Amosi
1 Awa ndi mawu a Amosi amene anali mmodzi mwa anthu oweta nkhosa ku Tekowa.+ Anauzidwa mawu amenewa m’masomphenya okhudza Isiraeli,+ m’masiku a Uziya+ mfumu ya Yuda ndi m’masiku a Yerobowamu+ mwana wa Yowasi,+ mfumu ya Isiraeli, zaka ziwiri chivomezi chisanachitike.+ 2 Iye anati:
“Yehova adzabangula ngati mkango mu Ziyoni,+ ndipo adzafuula mu Yerusalemu.+ Malo amene abusa amadyetserako ziweto adzalira, ndipo pansonga ya phiri la Karimeli padzauma.”+
3 “Yehova wanena kuti, ‘“Popeza kuti Damasiko+ anapanduka mobwerezabwereza,* sindidzamusinthira chigamulo changa. Sindidzamusinthira chigamulocho chifukwa chakuti anapuntha Giliyadi+ ndi zida zachitsulo zopunthira. 4 Ndidzatumiza moto+ panyumba ya Hazaeli,+ ndipo udzanyeketsa nsanja zokhalamo za Beni-hadadi.+ 5 Ndidzathyola mipiringidzo ya zipata za Damasiko+ ndi kupha anthu a ku Bikati-aveni. Ndidzaphanso munthu wogwira ndodo yachifumu wa ku Beti-edeni, ndipo anthu a ku Siriya adzatengedwa kupita ku ukapolo ku Kiri,”+ watero Yehova.’
6 “Yehova wanena kuti, ‘“Chifukwa chakuti Gaza wandipandukira mobwerezabwereza,+ sindidzamusinthira chigamulo changa. Sindidzamusinthira chigamulocho chifukwa chakuti anthu onse ogwidwa ukapolo+ anawapereka ku Edomu.+ 7 Ndidzatumiza moto pakhoma la Gaza+ ndipo udzanyeketsa nsanja zake zokhalamo. 8 Ndidzapha anthu a ku Asidodi+ pamodzi ndi wogwira ndodo yachifumu wa ku Asikeloni.+ Ndidzalanga+ Ekironi+ ndipo ndidzafafaniza otsala mwa Afilisiti,”+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.’
9 “Yehova wanena kuti, ‘Popeza kuti Turo+ anapanduka mobwerezabwereza, sindidzamusinthira chigamulo changa. Sindidzamusinthira chigamulocho chifukwa chakuti anapereka ku Edomu gulu lonse la anthu ogwidwa ukapolo, ndiponso chifukwa chakuti sanakumbukire pangano la pa ubale.+ 10 Ndidzatumiza moto pakhoma la Turo ndipo udzanyeketsa nsanja zake zokhalamo.’+
11 “Yehova wanena kuti, ‘Chifukwa chakuti Edomu wandipandukira mobwerezabwereza,+ sindidzamusinthira chigamulo changa. Sindidzamusinthira chigamulocho chifukwa chakuti anathamangitsa m’bale wake ndi lupanga,+ sanasonyeze chifundo,+ akupitiriza kukhadzulakhadzula zinthu ali wokwiya komanso akukhalabe wokwiya mosalekeza.+ 12 Ndidzatumiza moto ku Temani+ ndipo udzanyeketsa nsanja zokhalamo za ku Bozira.’+
13 “Yehova wanena kuti, ‘“Chifukwa chakuti ana a Amoni+ andipandukira mobwerezabwereza, sindidzawasinthira chigamulo changa.+ Sindidzawasinthira chigamulocho chifukwa chakuti anatumbula akazi apakati a ku Giliyadi ndi cholinga chakuti afutukule malo awo okhala.+ 14 Ndidzayatsa mpanda wa Raba+ ndipo motowo udzanyeketsa nsanja zake zokhalamo. Padzakhala chizindikiro chochenjeza pa tsiku la nkhondo ndiponso mphepo yamkuntho pa tsiku la chimvula champhamvu.+ 15 Pamenepo mfumu yawo idzagwidwa ndi kupita ku ukapolo pamodzi ndi akalonga ake,”+ watero Yehova.’