2 Mbiri
5 Pa mapeto pake, Solomo anamaliza ntchito yonse ya panyumba ya Yehova imene anayenera kugwira.+ Kenako Solomo anayamba kubweretsa zinthu zimene Davide bambo ake+ anaziyeretsa. Siliva, golide, ndi ziwiya zonse anaziika mosungira chuma cha panyumba ya Mulungu woona.+ 2 Pa nthawi imeneyo m’pamene Solomo anauza akulu a Isiraeli,+ mitu yonse ya mafuko,+ ndi atsogoleri a nyumba za makolo+ a ana a Isiraeli kuti asonkhane ku Yerusalemu. Anawauza kuti akatenge likasa+ la pangano la Yehova ku+ Mzinda wa Davide,+ kutanthauza Ziyoni.+ 3 Choncho anthu onse a mu Isiraeli anasonkhana kwa mfumu pachikondwerero cha m’mwezi wa 7.+
4 Akulu onse a Isiraeli anabwera,+ ndipo Alevi anayamba kunyamula Likasa.+ 5 Ansembe achilevi+ ananyamula Likasa,+ chihema chokumanako,+ ndi ziwiya zonse zopatulika+ zimene zinali m’chihemacho. 6 Mfumu Solomo ndi msonkhano wonse wa Aisiraeli, onse amene anabwera atawaitana, anafika pamaso pa Likasa n’kuyamba kupereka nsembe+ zambiri za nkhosa ndi ng’ombe, zomwe sanathe kuziwerenga chifukwa chochuluka. 7 Kenako ansembe anabweretsa likasa la pangano la Yehova kumalo ake, kuchipinda chamkati+ cha nyumbayo, Malo Oyera Koposa,+ ndipo analiika pansi pa mapiko a akerubi.+ 8 Mapiko a akerubiwo anali otambasukira pamwamba pa malo okhala Likasa, moti akerubiwo anatchinga pamwamba+ pa Likasa ndi pamwamba pa mitengo yake yonyamulira.+ 9 Koma mitengo yonyamulirayo inali yaitali, moti nsonga zake zinali kuonekera ku Malo Oyera kutsogolo kwa chipinda chamkati, koma sizinali kuoneka kunja. Mitengo yonyamulirayo ikadali pomwepo mpaka lero.+ 10 Mu Likasalo munalibe chilichonse kupatulapo miyala iwiri yosema+ imene Mose anaikamo ku Horebe.+ Anaiikamo nthawi imene Yehova anachita pangano+ ndi ana a Isiraeli, pamene anali kutuluka m’dziko la Iguputo.+
11 Tsopano ansembe anatuluka m’malo oyera (chifukwa ansembe onse amene analipo anali atadziyeretsa+ ndipo panalibe chifukwa choti atumikire motsatira magulu awo).+ 12 Ndipo Alevi+ oimba a m’gulu la Asafu,+ Hemani,+ Yedutuni,+ ana awo ndi abale awo, onsewa atavala zovala zabwino kwambiri atanyamula zinganga,+ zoimbira za zingwe+ ndi azeze,+ anaimirira kum’mawa kwa guwa lansembe pamodzi ndi ansembe okwanira 120 oimba malipenga.+ 13 Tsopano anthu oimba malipenga ndi oimba pakamwa anayamba kuimba mogwirizana+ n’kumamveka ngati mawu amodzi otamanda ndi kuthokoza Yehova. Komanso anayamba kuimba+ ndi malipenga, zinganga, ndi zoimbira zina potamanda+ Yehova ndi mawu akuti, “chifukwa iye ndi wabwino,+ pakuti kukoma mtima kwake kosatha+ kudzakhala mpaka kalekale.” Kenako mtambo unadzaza nyumbayo,+ nyumba ya Yehova.+ 14 Chifukwa cha mtambowo,+ ansembewo analephera kupitiriza kutumikira, popeza ulemerero+ wa Yehova unadzaza nyumba ya Mulungu woona.