MLALIKI
1 Mawu a wosonkhanitsa anthu,+ mwana wa Davide, mfumu ya ku Yerusalemu.+
3 Kodi munthu amapeza chiyani pa ntchito yake yonse yovuta
5 Dzuwa limatuluka* ndipo dzuwa limalowa,
Kenako limathamanga* kupita kumalo amene limatulukira kuti likatulukenso.+
6 Mphepo imapita kumʼmwera ndipo imazungulira mpaka kukafika kumpoto.
Imangozungulira mobwerezabwereza. Mphepoyo imapitiriza kuzungulira.
7 Mitsinje yonse* imakathira mʼnyanja koma nyanjayo sidzaza.+
Imabwerera kumalo kumene ikuchokera kuti ikayambirenso kuyenda.+
8 Zinthu zonse nʼzotopetsa.
Palibe aliyense amene angazifotokoze.
Diso silikhuta ndi kuona,
Ndipo khutu silidzaza chifukwa cha kumva.
9 Zimene zinalipo nʼzimene zidzakhaleponso,
Ndipo zimene zinachitidwa nʼzimene zidzachitidwenso.
Palibe chatsopano padziko lapansi pano.+
10 Kodi chilipo chimene munthu anganene kuti, “Wachiona ichi, nʼchatsopanotu chimenechi?”
Ayi, chakhalapo kuyambira kalekale.
Chinalipo kale ife tisanabadwe.
11 Palibe amene amakumbukira anthu akale.
Ndipo palibe amene adzakumbukire amene anabwera pambuyo pa anthu akalewo.
Iwowanso sadzakumbukiridwa ndi amene adzabwere pambuyo pawo.+
12 Ine wosonkhanitsa anthu, ndine mfumu ya Isiraeli ku Yerusalemu.+ 13 Ndinatsimikiza mumtima mwanga kuti ndiphunzire ndi kufufuza mwanzeru+ zonse zimene zachitidwa padziko lapansi.+ Ndinafufuza ntchito yotopetsa kwambiri imene Mulungu wapatsa ana a anthu kuti azigwira.
14 Ndinaona ntchito zonse zimene zinachitidwa padziko lapansi pano,
Ndipo ndinapeza kuti zonse ndi zachabechabe, zili ngati kuthamangitsa mphepo.+
15 Chinthu chokhota sichingawongoledwe,
Ndipo chimene palibe sichingawerengedwe nʼkomwe.
16 Choncho ndinanena mumtima mwanga kuti: “Ine ndapeza nzeru zambiri kuposa aliyense amene anakhalapo mu Yerusalemu+ ine ndisanakhalepo. Ndipo mtima wanga wamvetsa zinthu zambiri chifukwa cha nzeru ndi kudziwa zinthu.”+ 17 Ndinayesetsa ndi mtima wonse kuti ndidziwe nzeru, ndidziwe misala* komanso kuti ndidziwe uchitsiru.+ Koma zimenezinso zili ngati kuthamangitsa mphepo.
18 Chifukwa nzeru zikachuluka, zokhumudwitsa zimachulukanso,
Choncho amene amadziwa zinthu zambiri amakhalanso ndi zopweteka zambiri.+
2 Ine ndinadziuza mumtima mwanga kuti: “Ndiyesereko kuchita zinthu zosangalatsa* kuti ndione kuti zili ndi phindu lotani.” Koma ndinaona kuti zimenezinso zinali zachabechabe.
2 Ponena za kuseka ndinanena kuti, “Ndi misala!”
Ndipo ponena za zosangalatsa ndinanena kuti, “Zili ndi phindu lanji?”
3 Ndinayesapo kukhala wokonda kumwa vinyo,+ komabe ndinkaonetsetsa kuti ndikuchita zinthu mwanzeru. Ndinayesanso kuchita zinthu zopusa kuti ndione zinthu zabwino, zimene anthu akuyenera kuchita pa zaka zochepa zimene amakhala ndi moyo padziko lapansi pano. 4 Ndinagwira ntchito zikuluzikulu.+ Ndinamanga nyumba zambirimbiri.+ Ndinalima minda ya mpesa yambirimbiri.+ 5 Ndinakonza minda yokongola komanso malo odzalamo maluwa ndi mitengo. Ndipo ndinadzalamo mitengo ya zipatso zosiyanasiyana. 6 Ndinapanga madamu a madzi kuti ndizithirira mitengo imene inamera mʼnkhalango yanga. 7 Ndinali ndi antchito aamuna ndi aakazi+ komanso ndinali ndi antchito amene anabadwira mʼnyumba mwanga.* Ndinalinso ndi ziweto zochuluka zedi, ngʼombe ndi nkhosa.+ Zinali zambiri kuposa za onse amene anakhalapo mu Yerusalemu ine ndisanakhalepo. 8 Ndinapeza siliva ndi golide wambiri,+ chuma chimene mafumu amakhala nacho* ndiponso chimene chimapezeka mʼzigawo za dziko.+ Ndinali ndi oimba aamuna ndi aakazi. Ndinalinso ndi akazi ambiri, omwe amasangalatsa kwambiri mtima wa amuna. 9 Ndinali ndi zinthu zambiri kuposa aliyense amene anakhalapo mu Yerusalemu+ ine ndisanakhalepo. Ndipo ndinapitiriza kuchitabe zinthu mwanzeru.
10 Sindinadzimane chilichonse chimene mtima wanga unkalakalaka.*+ Mtima wanga sindinaumane zosangalatsa za mtundu uliwonse. Ndinkasangalala chifukwa cha ntchito yonse imene ndinagwira mwakhama. Imeneyi inali mphoto yanga* pa ntchito yonse imene ndinagwira mwakhama.+ 11 Koma nditaganizira ntchito zonse zimene manja anga anagwira ndiponso ntchito yovuta imene ndinachita khama kuti ndiikwanitse,+ ndinaona kuti zonse zinali zachabechabe, kunali ngati kuthamangitsa mphepo.+ Padziko lapansi pano panalibe chaphindu chilichonse.+
12 Kenako ndinayamba kuganizaganiza kuti nzeru nʼchiyani, misala nʼchiyani ndiponso kuti uchitsiru nʼchiyani.+ (Kodi munthu amene wabwera pambuyo pa mfumu angachite chiyani? Zimene angachite nʼzimene anthu ena anachita kale.) 13 Ndinaona kuti nzeru nʼzopindulitsa kuposa uchitsiru+ mofanana ndi mmene kuwala kulili kopindulitsa kuposa mdima.
14 Munthu wanzeru maso ake amaona bwino+ koma wopusa amayenda mumdima.+ Komanso ndazindikira kuti zimene zimachitikira onsewa nʼzofanana.+ 15 Choncho mumtima mwanga ndinanena kuti: “Zimene zimachitikira opusa inenso zidzandichitikira.”+ Ndiye ndinapindula chiyani chifukwa chokhala wanzeru kwambiri? Choncho mumtima mwanga ndinanena kuti: “Izinso nʼzachabechabe.” 16 Chifukwa munthu wanzeru komanso munthu wopusa,+ onsewa sadzakumbukiridwa mpaka kalekale. Mʼmasiku amene akubwerawa aliyense adzaiwalika. Ndipo kodi wanzeru adzafa bwanji? Adzafa mofanana ndi wopusa.+
17 Choncho ndinayamba kudana ndi moyo+ chifukwa ndinkaona kuti chilichonse chimene chikuchitika padziko lapansi pano chikupangitsa kuti ndizivutika mumtima. Chifukwa zonse zinali zachabechabe,+ zinali ngati kuthamangitsa mphepo.+ 18 Ndinayamba kudana ndi zinthu zonse zimene ndinapeza nditagwira ntchito mwakhama padziko lapansi pano,+ chifukwa ndidzayenera kusiyira munthu amene akubwera pambuyo panga.+ 19 Ndipo ndi ndani akudziwa ngati angadzakhale wanzeru kapena wopusa?+ Koma adzatenga zinthu zanga zonse zimene ndinapeza nditagwira ntchito mwakhama komanso mwanzeru padziko lapansi pano. Zimenezinso nʼzachabechabe. 20 Choncho ndinayamba kutaya mtima poganizira ntchito yanga yonse yovuta imene ndinagwira mwakhama padziko lapansi pano. 21 Chifukwa munthu akhoza kugwira ntchito mwakhama ndipo angachite zonse mwanzeru, mozindikira komanso mwaluso. Koma amayenerabe kupereka zonse zimene ali nazo kwa munthu amene sanagwire ntchito iliyonse kuti apeze zinthuzo.+ Zimenezinso nʼzachabechabe ndipo nʼzomvetsa chisoni kwambiri.*
22 Kodi munthu amapeza chiyani pa ntchito yonse imene wagwira mwakhama, chifukwa cha zimene amalakalaka mumtima mwake padziko lapansi pano?+ 23 Chifukwa masiku onse a moyo wake, ntchito yakeyo imamubweretsera zowawa ndi zokhumudwitsa.+ Ndipo ngakhale usiku mtima wake supuma.+ Izinso nʼzachabechabe.
24 Palibe chabwino kwa munthu kuposa kuti adye, amwe ndi kusangalala chifukwa choti wagwira ntchito mwakhama.+ Ndinazindikira kuti zimenezinso nʼzochokera mʼdzanja la Mulungu woona,+ 25 chifukwa ndi ndani amene amamwa ndi kudya bwino kuposa ine?+
26 Munthu amene amasangalatsa Mulungu, Mulunguyo amamʼpatsa nzeru ndi kudziwa zinthu komanso amamuchititsa kuti azisangalala.+ Koma munthu wochimwa amamʼpatsa ntchito yotuta ndi kusonkhanitsa zinthu kuti azipereke kwa munthu amene amasangalatsa Mulungu woona.+ Zimenezinso nʼzachabechabe, zili ngati kuthamangitsa mphepo.
3 Chilichonse chili ndi nthawi yake,
Pali nthawi yochitira chinthu chilichonse padziko lapansi:
2 Pali nthawi yobadwa ndi nthawi yakufa.
Nthawi yodzala ndi nthawi yozula chimene chinadzalidwa.
3 Nthawi yakupha ndi nthawi yochiritsa.
Nthawi yogumula ndi nthawi yomanga.
4 Nthawi yolira ndi nthawi yoseka.
Nthawi yolira mofuula ndi nthawi yovina.*
5 Nthawi yotaya miyala ndi nthawi younjika miyala pamodzi.
Nthawi yokumbatirana ndi nthawi yopewa kukumbatirana.
6 Nthawi yofunafuna ndi nthawi yovomereza kuti chinthu chatayika.
Nthawi yosunga ndi nthawi yotaya.
7 Nthawi yongʼamba+ ndi nthawi yosoka.
Nthawi yokhala chete+ ndi nthawi yolankhula.+
8 Nthawi yachikondi ndi nthawi yachidani.+
Nthawi yankhondo ndi nthawi yamtendere.
9 Kodi munthu wogwira ntchito amapeza phindu lanji pa ntchito yonse imene akugwira mwakhama?+ 10 Ndaona ntchito imene Mulungu wapatsa ana a anthu kuti azikhala ndi zochita. 11 Chilichonse iye anachipanga chokongola* ndiponso pa nthawi yake.+ Komanso anapatsa anthu mtima wofuna kukhala ndi moyo mpaka kalekale. Komabe anthu sadzadziwa ntchito imene Mulungu woona wagwira kuyambira pachiyambi mpaka pamapeto.
12 Ndazindikira kuti palibe chabwino kuposa kuti iwo asangalale ndiponso kuti azichita zabwino pamene ali ndi moyo,+ 13 komanso kuti munthu aliyense adye ndi kumwa nʼkumasangalala ndi zinthu zabwino, chifukwa cha ntchito yake yonse imene waigwira mwakhama. Imeneyi ndi mphatso yochokera kwa Mulungu.+
14 Ndazindikira kuti zonse zimene Mulungu woona amapanga zidzakhalapo mpaka kalekale. Palibe choti nʼkuwonjezerapo kapena kuchotsapo. Mulungu woona anazipanga mwanjira imeneyi kuti anthu azimuopa.+
15 Chilichonse chimene chikuchitika chinachitikapo kale ndipo zimene zidzachitike zinachitikapo kale.+ Koma Mulungu woona amafufuza zinthu zimene anthu akuzifunafuna.*
16 Ine ndaonanso zinthu izi padziko lapansi pano: Pamene panayenera kukhala chilungamo panali zoipa, ndipo pamene panayenera kuchitika zachilungamo panachitika zoipa.+ 17 Choncho mumtima mwanga ndinanena kuti: “Mulungu woona adzaweruza olungama ndi oipa omwe+ chifukwa pali nthawi yoyenera yoti chinthu chilichonse chichitike.”
18 Ndinanenanso mumtima mwanga zokhudza ana a anthu kuti Mulungu woona adzawayesa komanso kuwasonyeza kuti iwo ndi ofanana ndi nyama. 19 Chifukwa anthu ali ndi mapeto ndipo nyamanso zili ndi mapeto. Mapeto a zonsezi ndi ofanana.+ Nyama imafa ndipo munthunso amafa, zonsezi zili ndi mzimu wofanana.+ Choncho munthu saposa nyama, chifukwa zinthu zonse nʼzachabechabe. 20 Zonse zimapita kumalo amodzi.+ Zonse zinachokera kufumbi+ ndipo zonse zimabwerera kufumbi.+ 21 Ndi ndani akudziwa ngati mzimu wa anthu umakwera mʼmwamba ndiponso ngati mzimu wa zinyama umatsika pansi?+ 22 Ndinaona kuti palibe chabwino kuposa kuti munthu asangalale ndi ntchito yake+ chifukwa imeneyo ndi mphoto yake.* Nanga ndi ndani amene angamuchititse kuti aone zimene zidzachitike iye atafa.+
4 Ine ndinaganiziranso zinthu zonse zimene anthu amachita akamapondereza anzawo padziko lapansi pano. Ndinaona anthu oponderezedwa akugwetsa misozi, koma panalibe aliyense woti awatonthoze.+ Anthu oponderezawo anali ndi mphamvu, moti panalibe aliyense woti atonthoze anthu oponderezedwawo. 2 Ndinazindikira kuti anthu amene anafa kale ali bwino kuposa anthu amene ali ndi moyo.+ 3 Koma amene ali bwino kwambiri kuposa onsewa ndi amene sanabadwe,+ amene sanaone zinthu zoipa zimene zikuchitika padziko lapansi pano.+
4 Ndaona kuti anthu akamagwira ntchito mopikisana, amaigwira mwakhama ndiponso mwaluso kwambiri.+ Izinso nʼzachabechabe ndipo zili ngati kuthamangitsa mphepo.
5 Wopusa amapinda manja ake osagwira ntchito ndipo amadzibweretsera mavuto.*+
6 Ndi bwino kupuma pangʼono* kusiyana nʼkugwira ntchito mwakhama* ndi kuthamangitsa mphepo.+
7 Ndinaganiziranso zinthu zina zachabechabe zimene zimachitika padziko lapansi pano: 8 Pali munthu amene ali yekhayekha, wopanda mnzake. Alibe mwana kapena mchimwene wake, koma amangokhalira kugwira ntchito mwakhama. Maso ake sakhutira ndi chuma.+ Koma kodi amadzifunsa kuti, “Ndikamagwira ntchito mwakhama komanso kudzimana zinthu zabwino, kodi ndikufuna kuti zinthu zimenezi adzasangalale nazo ndani?”+ Izinso nʼzachabechabe ndipo ndi ntchito yobweretsa nkhawa.+
9 Awiri amaposa mmodzi+ chifukwa amapeza mphoto yabwino* pa ntchito yawo imene amaigwira mwakhama. 10 Chifukwa ngati mmodzi wa iwo atagwa, winayo akhoza kuthandiza mnzakeyo kuti adzuke. Koma kodi chingachitike nʼchiyani kwa munthu amene wagwa koma palibe woti amuthandize kuti adzuke?
11 Komanso anthu awiri akagona pamodzi amamva kutentha. Koma kodi mmodzi yekha angamve bwanji kutentha? 12 Munthu akhoza kugonjetsa munthu mmodzi koma anthu awiri akhoza kulimbana naye. Ndipo chingwe chopotedwa ndi zingwe zitatu sichingaduke msanga.*
13 Mwana wosauka koma wanzeru ali bwino kuposa mfumu yokalamba koma yopusa,+ imene sionanso kufunika komvera chenjezo.+ 14 Chifukwa mwanayo amatuluka mʼndende nʼkukhala mfumu+ ngakhale kuti anabadwa ali wosauka mu ufumuwo.+ 15 Ndinaganizira za anthu onse amoyo amene amayenda padziko lapansi pano komanso za mmene zimakhalira ndi wachinyamata amene amalowa mʼmalo mwa mfumu. 16 Ngakhale kuti anthu amene ali kumbali yake ndi ambiri, anthu obwera pambuyo pake sadzasangalala naye.+ Izinso nʼzachabechabe ndipo zili ngati kuthamangitsa mphepo.
5 Uzisamala mmene ukuyendera ukapita kunyumba ya Mulungu woona.+ Ndi bwino kuti ukapita kumeneko uzikamvetsera,+ kusiyana ndi kukapereka nsembe ngati mmene anthu opusa amachitira+ chifukwa iwo sakudziwa kuti zimene akuchita nʼzoipa.
2 Usamapupulume kulankhula kapena kulola kuti mtima wako ufulumire kulankhula pamaso pa Mulungu woona,+ chifukwa Mulungu woona ali kumwamba koma iwe uli padziko lapansi. Nʼchifukwa chake suyenera kulankhula zambiri.+ 3 Maloto amabwera chifukwa chochuluka zochita,*+ ndipo munthu wopusa akamalankhula zinthu zambiri, zimachititsa kuti alankhule zinthu zopanda pake.+ 4 Ukalonjeza kwa Mulungu usamachedwe kukwaniritsa lonjezo lako,+ chifukwa Mulungu sasangalala ndi anthu opusa.+ Uzikwaniritsa zinthu zimene walonjeza.+ 5 Ndi bwino kuti usalonjeze kusiyana ndi kulonjeza koma osakwaniritsa zimene walonjezazo.+ 6 Usalole kuti pakamwa pako pakuchimwitse,+ komanso usamauze mngelo* kuti unalakwitsa.+ Nʼchifukwa chiyani ukufuna kukwiyitsa Mulungu woona ndi zonena zako mpaka kufika poti awononge ntchito ya manja ako?+ 7 Pajatu zochita zikachuluka zimachititsa kuti munthu azingolota.+ Mofanana ndi zimenezi, mawu akachuluka zotsatira zake zimakhala zachabechabe. Koma uziopa Mulungu woona.+
8 Ukaona munthu wosauka akuponderezedwa ndiponso zinthu zopanda chilungamo zikuchitika mʼdera limene ukukhala, usadabwe nazo.+ Chifukwa munthu waudindoyo akuonedwa ndi wina waudindo waukulu kuposa iyeyo. Ndipo pali enanso amene ali ndi udindo waukulu kuposa onsewo.
9 Komanso, onsewo amapindula ndi zimene dzikoli limatulutsa. Ngakhale zimene mfumu imadya zimachokera kumunda.+
10 Munthu wokonda siliva sakhutira ndi siliva, ndipo wokonda chuma sakhutira ndi phindu limene amapeza.+ Zimenezinso nʼzachabechabe.+
11 Zinthu zabwino zikachuluka ozidya amachulukanso.+ Ndipo kodi mwiniwake wa zinthuzo amapindula chiyani kuposa kumangoziyangʼana ndi maso ake?+
12 Wotumikira munthu wina amagona tulo tokoma, kaya adye zochepa kapena zambiri. Koma zambiri zimene munthu wolemera amakhala nazo zimamulepheretsa kugona.
13 Pali chinthu* chomvetsa chisoni kwambiri chimene ndaona padziko lapansi pano: Munthu ankangosonkhanitsa chuma koma pambuyo pake chinamupweteketsa. 14 Chumacho chinatha chifukwa cha zinthu zina* zimene sizinayende bwino, ndipo atabereka mwana, analibe chilichonse choti amusiyire ngati cholowa.+
15 Monga mmene munthu anabadwira kuchokera mʼmimba mwa mayi ake, adzapitanso wamaliseche ngati mmene anabwerera.+ Ndipo sangatenge chilichonse pa ntchito yake imene anaigwira mwakhama.+
16 Palinso chinthu china chomvetsa chisoni kwambiri:* Monga mmene munthu anabwerera, adzapitanso chimodzimodzi. Ndipo kodi munthu amene amagwira ntchito mwakhama koma zonse nʼkungopita ndi mphepo amapindula chiyani?+ 17 Komanso, tsiku lililonse amadya chakudya chake mumdima ndipo amakhala ndi nkhawa zambiri, amadwala komanso amakhala wokwiya.+
18 Chinthu chabwino kwambiri ndiponso choyenera chimene ine ndaona nʼchakuti: Munthu ayenera kudya, kumwa ndi kusangalala+ chifukwa cha ntchito yake yonse yovuta imene amaigwira mwakhama padziko lapansi pano, kwa masiku ochepa a moyo wake amene Mulungu woona wamupatsa. Chifukwa imeneyo ndi mphoto yake.*+ 19 Komanso Mulungu woona akapatsa munthu chuma ndiponso zinthu zambiri+ zimene angathe kusangalala nazo, ayenera kulandira mphoto yake* ndi kusangalala chifukwa cha ntchito imene waigwira mwakhama. Imeneyi ndi mphatso yochokera kwa Mulungu.+ 20 Adzaona kuti masiku a moyo wake akudutsa mofulumira kwambiri, chifukwa Mulungu woona adzamuchititsa kuti akhale wotanganidwa ndi zinthu zimene mtima wake umasangalala nazo.+
6 Pali chinthu chinanso chomvetsa chisoni chimene* ndaona padziko lapansi pano ndipo nʼchofala pakati pa anthu: 2 Mulungu woona amapatsa munthu chuma, katundu ndi ulemerero moti sasowa chilichonse chimene amalakalaka. Komabe Mulungu woona samulola kuti asangalale ndi zinthu zimenezi ngakhale kuti munthu wina angathe kusangalala nazo. Zimenezi nʼzachabechabe komanso tsoka lalikulu. 3 Ngati munthu atabereka ana 100 nʼkukhala ndi moyo zaka zambirimbiri mpaka kukalamba, koma osasangalala ndi zinthu zabwino zimene ali nazo asanalowe mʼmanda, ndithu mwana amene anabadwa wakufa ali bwino kuposa iyeyu.+ 4 Chifukwa kubadwa kwa mwanayu kunali kopanda phindu. Zinali ngati kuti wafera mumdima ndipo alibe dzina. 5 Ngakhale kuti mwanayu sanaone dzuwa kapena kudziwa chilichonse, ali bwinobe* kuposa munthu woyamba uja.+ 6 Kodi pali phindu lanji ngati munthu atakhala ndi moyo zaka 1,000 kapena 2,000 koma osasangalala ndi moyo? Kodi si paja anthu onse amapita kumalo amodzi?+
7 Ntchito yonse imene munthu amagwira mwakhama amagwirira pakamwa pake,+ koma zolakalaka zake sizitha. 8 Kodi pali ubwino wotani kukhala munthu wanzeru kusiyana ndi kukhala munthu wopusa?+ Kapena kodi pali phindu lanji kuti munthu wosauka amadziwa zimene angachite kuti akhale ndi moyo?* 9 Ndi bwino kusangalala ndi zinthu zimene maso ako akuona kuposa kulakalaka zinthu zimene sungazipeze.* Izinso nʼzachabechabe ndipo zili ngati kuthamangitsa mphepo.
10 Chilichonse chimene chinakhalapo chinapatsidwa kale dzina ndipo nʼzodziwika kuti munthu ndi ndani. Iye sangathe kutsutsana* ndi amene ali wamphamvu kuposa iyeyo. 11 Mawu akachuluka* zinthu zachabechabe zimachulukanso, ndiye kodi munthu zimamupindulitsa chiyani? 12 Ndi ndani akudziwa zinthu zabwino zimene munthu angachite pa masiku ochepa a moyo wake wachabechabe, umene umakhala ngati mthunzi?+ Chifukwa ndi ndani angauze munthu zimene zidzachitike padziko lapansi pano iyeyo atafa?
7 Mbiri yabwino imaposa* mafuta amtengo wapatali,+ ndipo tsiku lomwalira limaposa tsiku lobadwa. 2 Ndi bwino kupita kunyumba yamaliro kusiyana ndi kupita kunyumba yamadyerero,+ chifukwa amenewo ndi mapeto a munthu aliyense, ndipo amene ali ndi moyo aziganizira zimenezi mumtima mwake. 3 Ndi bwino kumva chisoni kusiyana ndi kuseka,+ chifukwa chisoni chimachititsa kuti munthu akhale ndi mtima wabwino.+ 4 Munthu wanzeru amene ali mʼnyumba yamaliro, amaganizira mozama za moyo ndi imfa. Koma munthu wopusa, nthawi zonse amaganizira za zisangalalo.+
5 Ndi bwino kumvetsera munthu wanzeru akamakudzudzula,+ kusiyana ndi kumvetsera nyimbo ya zitsiru. 6 Kuseka kwa anthu opusa kuli ngati kuthetheka kwa minga zomwe zikuyaka pansi pa mphika.+ Zimenezinso nʼzachabechabe. 7 Koma kuponderezedwa kungapangitse munthu wanzeru kuchita zinthu ngati wamisala, ndipo chiphuphu chimawononga mtima wa munthu.+
8 Mapeto a chinthu amakhala bwino kuposa chiyambi chake. Ndipo kukhala woleza mtima ndi kwabwino kuposa kukhala wodzikuza.+ 9 Usamafulumire kukwiya,+ chifukwa anthu opusa ndi amene sachedwa kukwiya.*+
10 Usanene kuti, “Nʼchifukwa chiyani kale zinthu zinali bwino kuposa masiku ano?” chifukwa si nzeru kufunsa funso ngati limeneli.+
11 Munthu wanzeru akalandira cholowa zimakhala bwino, ndipo nzeru zimapindulitsa anthu amene ali padziko lapansi.* 12 Chifukwa nzeru zimateteza+ mofanana ndi mmene ndalama zimatetezera.+ Koma ubwino wa kudziwa zinthu ndi uwu: Nzeru zimateteza moyo wa amene ali ndi nzeruzo.+
13 Ganizira ntchito ya Mulungu woona, chifukwa ndi ndani amene angathe kuwongola zinthu zimene iye anazikhotetsa?+ 14 Pa tsiku labwino, uzichitanso zinthu zabwino.+ Koma pa tsiku latsoka uzikumbukira kuti Mulungu woona anapanga masiku onsewa+ nʼcholinga choti anthu asamadziwe chilichonse chimene chidzawachitikire mʼtsogolo.+
15 Pa moyo wanga wopanda pakewu,+ ndaona chilichonse. Ndaona munthu wolungama amene amawonongeka akuchita zinthu zolungama,+ komanso ndaona munthu woipa amene amakhala ndi moyo wautali ngakhale kuti akuchita zoipa.+
16 Usakhale wolungama mopitirira muyezo+ kapena kudzionetsera kuti ndiwe wanzeru kwambiri.+ Nʼchifukwa chiyani ukufuna kudzibweretsera mavuto?+ 17 Usakhale woipa mopitirira muyezo kapena kukhala wopusa.+ Uferenji mwamsanga?+ 18 Ndi bwino kwambiri kuti usunge malangizo onsewa, usasiyepo ena.+ Chifukwa munthu amene amaopa Mulungu adzamvera malangizo onsewa.
19 Nzeru zimapangitsa kuti munthu wanzeru akhale wamphamvu kwambiri kuposa amuna 10 amphamvu amene ali mumzinda.+ 20 Chifukwa padziko lapansi palibe munthu wolungama amene amachita zabwino nthawi zonse ndipo sachimwa.+
21 Komanso usamaganizire kwambiri mawu aliwonse amene anthu akulankhula.+ Ukamachita zimenezi ukhoza kumva wantchito wako akukunenera zoipa,* 22 chifukwa iweyo ukudziwa bwino mumtima mwako kuti wanenerapo anthu ena zoipa kambirimbiri.+
23 Ndinaganizira zinthu zonsezi mwanzeru ndipo ndinati: “Ndidzakhala wanzeru.” Koma zinali zosatheka kuti ndipeze nzeruzo. 24 Zimene zinachitika kale sitingathe kuzimvetsa ndipo nʼzozama kwambiri. Ndi ndani angazimvetse?+ 25 Mumtima mwanga ndinasankha kuti ndidziwe, ndifufuze ndiponso ndifunefune nzeru komanso chifukwa chake zinthu zinazake zimachitika. Ndinafunanso kumvetsa kuti uchitsiru ndi woipa bwanji komanso makhalidwe opusa a anthu amene amachita zinthu ngati amisala.+ 26 Ndiye ndinapeza izi: Mkazi amene ali ngati ukonde wosakira nyama, amene mtima wake uli ngati khoka, komanso amene manja ake ali ngati unyolo wakundende, ndi wowawa kwambiri kuposa imfa. Munthu amene amasangalatsa Mulungu woona adzamuthawa,+ koma wochimwa amagwidwa naye.+
27 Wosonkhanitsa anthu akunena kuti: “Taona, izi ndi zimene ndapeza.+ Ndafufuza chinthu chimodzi ndi chimodzi kuti ndidziwe zimenezi, 28 koma chimene ndinkachifufuza kwambiri sindinachipeze. Pa anthu 1,000, ndinapezapo mwamuna mmodzi yekha wolungama,* koma pa anthu onsewa sindinapezepo mkazi wolungama. 29 Zimene ndapeza ndi izi zokha: Mulungu woona anapanga anthu owongoka mtima,+ koma anthuwo asankha kuchita zinthu zogwirizana ndi zolinga zawo.”+
8 Ndi ndani angafanane ndi munthu wanzeru? Ndipo ndi ndani akudziwa njira yothetsera vuto?* Nzeru za munthu zimachititsa nkhope yake kuwala ndipo nkhope yake yokwiya imasintha nʼkumaoneka bwino.
2 Ndikunena kuti: “Uzimvera malamulo a mfumu+ polemekeza lumbiro limene unachita kwa Mulungu.+ 3 Usafulumire kuchoka pamaso pake,+ ndipo usayambe kuchita nawo zinthu zoipa.+ Chifukwa mfumuyo ikhoza kuchita chilichonse chimene ikufuna kuchita, 4 popeza mfumu ili ndi mphamvu yolamula.+ Ndipo ndi ndani angaifunse kuti, ‘Kodi mukuchita chiyani?’”
5 Munthu amene amatsatira malamulo sadzakumana ndi mavuto,+ ndipo munthu wa mtima wanzeru amadziwa nthawi yoyenera komanso njira yoyenera yochitira zinthu.+ 6 Chifukwa mavuto a anthu ndi ambiri, zinthu zonse zizichitidwa mʼnjira yoyenera komanso pa nthawi yoyenera.+ 7 Popeza palibe aliyense akudziwa zimene zidzachitike, ndiye ndi ndani angamuuze mmene zidzachitikire?
8 Palibe munthu amene ali ndi mphamvu pa mzimu* kapena amene angaletse mzimuwo kuti usachoke. Mofanana ndi zimenezi palibenso amene ali ndi mphamvu pa tsiku la imfa.+ Palibe amene amaloledwa kuchoka kunkhondo ndipo mofanana ndi zimenezi, anthu amene amachita zoipa, kuipako sikudzawalola kuti athawe.*
9 Zonsezi ndaziona ndipo mtima wanga unaganizira za ntchito iliyonse imene yachitidwa padziko lapansi pano, pa nthawi imene munthu wapweteka munthu mnzake pomulamulira.+ 10 Ndaona anthu oipa akuikidwa mʼmanda, amene ankalowa ndi kutuluka mʼmalo oyera, koma sanachedwe kuiwalika mumzinda umene ankachitiramo zinthu zoipa.+ Izinso nʼzachabechabe.
11 Chifukwa anthu ochita zoipa sanalangidwe mwamsanga,+ anthu atsimikiza mtima kuchita zoipa.+ 12 Ngakhale woipa atachita zoipa maulendo 100 nʼkukhalabe ndi moyo wautali, ine ndikudziwa kuti anthu amene amaopa Mulungu woona zidzawayendera bwino, chifukwa chakuti amamuopa.+ 13 Koma woipayo sizidzamuyendera bwino+ ndipo sadzatalikitsa moyo wake umene uli ngati mthunzi,+ chifukwa saopa Mulungu.
14 Pali chinthu china chachabechabe* chimene chimachitika padziko lapansi: Pali anthu olungama amene amachitiridwa zinthu ngati kuti achita zoipa,+ ndipo pali anthu oipa amene amachitiridwa zinthu ngati kuti achita zachilungamo.+ Ndikunena kuti zimenezinso nʼzachabechabe.
15 Choncho ndinauza anthu kuti ndi bwino kusangalala+ chifukwa palibe chabwino kwa munthu padziko lapansi pano kuposa kudya, kumwa ndi kusangalala. Azichita zimenezi pamene akugwira ntchito mwakhama masiku onse a moyo wake,+ amene Mulungu woona wamupatsa padziko lapansi pano.
16 Ndinatsimikiza mumtima mwanga kuti ndipeze nzeru ndiponso kuti ndione zinthu zonse* zimene zikuchitika padziko lapansi,+ mpaka kufika pomasala tulo masana ndi usiku.* 17 Ndiyeno ndinaganizira ntchito yonse ya Mulungu woona, ndipo ndinazindikira kuti anthu sangamvetse zimene zimachitika padziko lapansi pano.+ Ngakhale anthu atayesetsa bwanji sangathe kuzimvetsa. Ngakhale atanena kuti ndi anzeru kwambiri ndipo zonsezi akuzidziwa, sangathebe kuzimvetsa.+
9 Choncho ndinaganizira zinthu zonsezi mumtima mwanga ndipo ndinaona kuti anthu olungama, anthu anzeru limodzi ndi ntchito zawo ali mʼmanja mwa Mulungu woona.+ Anthu sakudziwa za chikondi kapena chidani chimene chinalipo iwo asanakhalepo. 2 Anthu onse mapeto awo ndi ofanana,+ munthu wolungama komanso munthu woipa,+ munthu wabwino ndi woyera komanso munthu wodetsedwa, munthu amene amapereka nsembe komanso amene sapereka nsembe. Munthu wabwino nʼchimodzimodzi ndi munthu wochimwa. Munthu amene amachita lumbiro nʼchimodzimodzi ndi amene amaganiza kaye asanachite lumbiro. 3 Chinthu chomvetsa chisoni chimene chimachitika padziko lapansi pano ndi ichi: Chifukwa chakuti mapeto a anthu onse ndi ofanana,+ mitima ya anthu ndi yodzaza ndi zoipa. Mumtima mwawo mumakhala misala pa nthawi imene ali ndi moyo ndipo kenako amafa.
4 Aliyense amene ali pakati pa anthu amoyo ali ndi chiyembekezo, chifukwa galu wamoyo ali bwino kuposa mkango wakufa.+ 5 Chifukwa amoyo amadziwa kuti adzafa,+ koma akufa sadziwa chilichonse+ komanso salandira mphoto iliyonse,* chifukwa zonse zimene anthu akanawakumbukira nazo zimaiwalika.+ 6 Komanso chikondi chawo, chidani chawo ndi nsanje yawo zatha kale, ndipo alibenso gawo lililonse pa zimene zikuchitika padziko lapansi pano.+
7 Pita ukadye chakudya chako mokondwera ndipo ukamwe vinyo wako ndi mtima wosangalala,+ chifukwa Mulungu woona wasangalala kale ndi ntchito zako.+ 8 Nthawi zonse zovala zako zizikhala zoyera* ndipo usamalephere kudzola mafuta kumutu kwako.+ 9 Sangalala ndi moyo limodzi ndi mkazi wako amene umamukonda+ masiku onse a moyo wako wachabechabe, amene Mulungu wakupatsa padziko lapansi pano. Usangalale masiku ako onse achabechabe, chifukwa imeneyi ndi mphoto imene* ukuyenera kulandira pa moyo wako komanso pa ntchito yovuta imene ukuigwira mwakhama padziko lapansi pano.+ 10 Chilichonse chimene dzanja lako lapeza kuti lichite, uchichite ndi mphamvu zako zonse, chifukwa ku Manda*+ kumene ukupitako kulibe kugwira ntchito, kuganiza zochita, kudziwa zinthu kapena nzeru.
11 Ndaonanso chinthu china padziko lapansi pano kuti si nthawi zonse pamene anthu othamanga kwambiri amapambana pampikisano komanso pamene amphamvu amapambana pankhondo.+ Si nthawi zonse pamene anthu ochenjera amapeza chakudya, ndiponso si nthawi zonse pamene anthu anzeru amakhala ndi chuma.+ Komanso anthu odziwa zinthu, si nthawi zonse pamene zinthu zimawayendera bwino,+ chifukwa nthawi yatsoka komanso zinthu zosayembekezereka zimagwera onsewo. 12 Chifukwa munthu sadziwa nthawi imene tsoka lingamugwere.+ Mofanana ndi nsomba zimene zimagwidwa mu ukonde wakupha, komanso mbalame zimene zimagwidwa mumsampha, ana a anthu nawonso amakodwa pa nthawi yatsoka, tsokalo likawagwera mwadzidzidzi.
13 Padziko lapansi pano ndinaonaponso zinthu izi zokhudza nzeru ndipo ndinagoma nazo: 14 Panali mzinda winawake waungʼono ndipo munali amuna ochepa. Kenako kunabwera mfumu yamphamvu ndipo inazungulira mzindawo nʼkuunjika milu ikuluikulu yadothi yoti imenyerepo nkhondo. 15 Mumzindawo munali munthu wosauka koma wanzeru ndipo anapulumutsa mzindawo chifukwa cha nzeru zakezo. Koma palibe aliyense amene anakumbukira munthu wosaukayo.+ 16 Choncho ndinaganiza kuti: ‘Nzeru nʼzabwino kuposa mphamvu,+ koma anthu amanyoza nzeru za munthu wosauka ndipo samvera mawu ake.’+
17 Ndi bwino kumvera mawu odekha a munthu wanzeru kusiyana ndi mawu ofuula a munthu amene akulamulira pakati pa anthu opusa.
18 Nzeru nʼzabwino kuposa zida zankhondo, koma wochimwa mmodzi yekha akhoza kuwononga zabwino zochuluka.+
10 Ntchentche zakufa nʼzimene zimachititsa kuti mafuta a munthu wopanga mafuta onunkhira awole nʼkuyamba kununkha. Mofanana ndi zimenezi uchitsiru pangʼono umawononga mbiri ya munthu amene amaoneka kuti ndi wanzeru komanso wolemekezeka.+
2 Mtima wa munthu wanzeru umamutsogolera njira yoyenera,* koma mtima wa munthu wopusa umamutsogolera njira yolakwika.*+ 3 Mʼnjira iliyonse imene munthu wopusa amayenda, amachita zinthu mopanda nzeru,*+ ndipo amaonetsetsa kuti aliyense adziwe kuti iye ndi wopusa.+
4 Mkwiyo* wa mtsogoleri ukakuyakira, usachoke pamalo ako,+ chifukwa kudekha kumachepetsa machimo aakulu.+
5 Pali chinthu china chomvetsa chisoni chimene ndaona padziko lapansi pano, zinthu zimene olamulira amalakwitsa:+ 6 Zitsiru zaikidwa pamaudindo ambiri akuluakulu, koma anthu oyenerera* amangokhala pamalo otsika.
7 Ndaonapo antchito atakwera pamahatchi, koma akalonga akuyenda wapansi ngati antchito.+
8 Amene akukumba dzenje angathe kugweramo+ ndipo amene akugumula mpanda wamiyala angathe kulumidwa ndi njoka.
9 Amene akuphwanya miyala, akhoza kudzipweteka nayo ndipo amene akuwaza nkhuni akhoza kuvulazidwa nazo.*
10 Ngati nkhwangwa yabunthwa ndipo munthu sanainole, adzafunika kugwiritsa ntchito mphamvu zambiri. Koma nzeru zimathandiza kuti zinthu ziyende bwino.
11 Njoka ikaluma munthu asanainyengerere bwinobwino kuti aiseweretse, ndiye kuti luso la katswiri woseweretsa njokayo lilibe phindu.
12 Mawu otuluka mʼkamwa mwa munthu wanzeru amakhala osangalatsa,+ koma milomo ya munthu wopusa imamubweretsera mavuto.+ 13 Mawu oyamba otuluka mʼkamwa mwake amakhala opusa+ ndipo mawu ake omaliza amakhala misala yobweretsa chiwonongeko. 14 Ngakhale zili choncho, munthu wopusa amangolankhulabe.+
Munthu sadziwa chimene chidzachitike. Ndi ndani amene angamuuze zimene zidzachitike iye atafa?+
15 Ntchito imene munthu wopusa amagwira mwakhama imamutopetsa, chifukwa sadziwa nʼkomwe njira yopitira mumzinda.
16 Zimakhala zomvetsa chisoni ngati mfumu imene ikulamulira mʼdziko ndi mnyamata+ ndipo ngati akalonga ake amayamba mʼmawa kuchita madyerero. 17 Zimakhala zosangalatsa ngati mfumu imene ikulamulira mʼdziko ndi mwana wochokera kubanja lachifumu ndipo akalonga amadya pa nthawi yake kuti apeze mphamvu, osati nʼcholinga choti aledzere.+
18 Chifukwa cha ulesi waukulu denga limaloshoka, ndipo chifukwa cha kuchita manja lende nyumba imadontha.+
19 Chakudya chimachititsa kuti anthu aziseka, ndipo vinyo amachititsa kuti moyo ukhale wosangalatsa,+ koma ndalama zimathandiza munthu kupeza chilichonse chimene akufuna.+
20 Ngakhale mʼmaganizo mwako,* usatemberere* mfumu+ ndipo usatemberere munthu wolemera kuchipinda kwako. Chifukwa mbalame* ikhoza kutenga mawu ako* kapena cholengedwa chokhala ndi mapiko chikhoza kukaulula zimene wanenazo.
11 Ponya* mkate wako pamadzi+ chifukwa pakapita masiku ambiri udzaupezanso.+ 2 Pereka gawo la zinthu zimene uli nazo kwa anthu 7 kapena 8+ chifukwa sukudziwa tsoka limene lidzagwe padziko lapansi.
3 Mitambo ikadzaza madzi, imakhuthulira mvula yochuluka padziko lapansi, ndipo mtengo ukagwera kumʼmwera kapena kumpoto, pamene wagwerapo udzakhala pomwepo.
4 Munthu amene amayangʼana mphepo sadzadzala mbewu ndipo amene amayangʼana mitambo sadzakolola.+
5 Iwe sudziwa mmene mzimu umachititsira kuti mafupa a mwana amene ali mʼmimba mwa mayi ake akule.+ Mofanana ndi zimenezi sudziwanso ntchito ya Mulungu woona, amene amachita zinthu zonse.+
6 Dzala mbewu zako mʼmawa ndipo dzanja lako lisapume mpaka madzulo,+ chifukwa sukudziwa zimene zidzachite bwino, kaya izi kapena zinazo, kapenanso ngati zonse zidzachite bwino.
7 Kuwala nʼkokoma ndipo ndi bwino kuti maso aone dzuwa. 8 Ngati munthu atakhala ndi moyo zaka zambiri, azisangalala pa zaka zonsezo.+ Koma azikumbukira kuti masiku a mdima akhoza kukhala ambiri. Zonse zimene zikubwera nʼzachabechabe.+
9 Mnyamata iwe, sangalala pa nthawi imene uli wachinyamata, ndipo mtima wako usangalale masiku a unyamata wako. Uzichita zimene mtima wako ukufuna ndipo uzipita kumene maso ako akukutsogolera. Koma dziwa kuti Mulungu woona adzakuweruza* pa zinthu zonsezi.+ 10 Choncho chotsa zinthu zobweretsa mavuto mumtima mwako ndipo teteza thupi lako ku zinthu zimene zingakuvulaze, chifukwa unyamata ndiponso pachimake pa moyo nʼzachabechabe.+
12 Choncho kumbukira Mlengi wako Wamkulu masiku a unyamata wako,+ asanafike masiku oipa*+ komanso zisanafike zaka zimene udzanena kuti: “Moyo sukundisangalatsa.” 2 Uchite zimenezi kuwala kwa dzuwa, mwezi ndi nyenyezi kusanazime+ ndiponso mitambo yamvula isanabwererenso pambuyo poti mvula yagwa. 3 Pa nthawi imeneyo olondera* nyumba adzayamba kunjenjemera, amuna amphamvu adzapindika, akazi adzasiya kupera ufa chifukwa adzatsala ochepa ndipo akazi oyangʼana pawindo azidzaona mdima.+ 4 Zitseko zotulukira popita mumsewu zidzatsekedwa, phokoso la miyala yoperera ufa lidzayamba kumveka motsika ndipo munthu azidzadzuka ndi kulira kwa mbalame, ndiponso ana onse aakazi azidzaimba nyimbo ndi mawu ofooka.+ 5 Komanso munthu azidzaopa malo okwera ndipo azidzadera nkhawa zinthu zoopsa mumsewu. Mtengo wa amondi udzachita maluwa,+ chiwala chizidzayenda mochita kudzikoka ndipo zakudya sizidzakoma,* chifukwa munthu adzakhala akupita kunyumba yake yokhalitsa+ ndipo olira azidzangoyendayenda mumsewu.+ 6 Uzikumbukira Mlengi wako chingwe chasiliva chisanachotsedwe, mbale yagolide isanaphwanyidwe, mtsuko umene uli pakasupe usanaphwanyike ndiponso wilo lotungira madzi pachitsime lisanathyoke. 7 Kenako fumbi lidzabwerera kunthaka+ kumene linali, ndipo mzimu* udzabwerera kwa Mulungu woona amene anaupereka.+
8 Wosonkhanitsa anthu akunena kuti:+ “Nʼzachabechabe!* Zinthu zonse nʼzachabechabe.”+
9 Kuwonjezera pa kukhala ndi nzeru, wosonkhanitsa anthuyu nthawi zonse ankaphunzitsa anthuwo zimene iye ankadziwa+ ndipo anaganizira mozama komanso anafufuza zinthu mosamala kuti alembe* miyambi yambiri.+ 10 Wosonkhanitsa anthuyu anafufuza mawu osangalatsa+ ndipo analemba mawu olondola a choonadi.
11 Mawu a anthu anzeru ali ngati zisonga zobayira ngʼombe pozitsogolera,+ ndipo mawu awo osankhidwa bwino ali ngati misomali imene aikhomerera kwambiri. Mawuwo aperekedwa ndi mʼbusa mmodzi. 12 Mwana wanga, ponena za zinthu zina kupatula izi, ndikukuchenjeza kuti: Anthu adzapitirizabe kulemba mabuku ambiri ndipo kuwawerenga kwambiri kumangotopetsa munthu.+
13 Poti zonse zanenedwa, mfundo yaikulu ndi yakuti: Opa Mulungu woona+ ndi kusunga malamulo ake+ chifukwa zimenezi ndi zimene munthu akuyenera kuchita.+ 14 Chifukwa Mulungu woona adzaweruza chilichonse chimene anthu amachita kuphatikizapo chinthu chilichonse chobisika, kuti aone ngati chili chabwino kapena choipa.+
Mʼchilankhulo choyambirira, “pansi pa dzuwa.”
Kapena kuti, “limawala.”
Kapena kuti, “limabwerera mwawefuwefu.”
Kapena kuti, “Mitsinje imene imayenda nthawi yamvula yokha.”
Kapena kuti, “uchitsiru wopitirira muyezo.”
Kapena kuti, “Ndiyesereko kusangalala.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ndinali ndi ana aamuna a mʼnyumba mwanga.”
Kapena kuti, “katundu amene amapezeka ndi mafumu okha.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “chimene maso anga anapempha.”
Kapena kuti, “Limeneli linali gawo langa.”
Kapena kuti, “ndipo ndi tsoka lalikulu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “nthawi yodumphadumpha mosangalala.”
Kapena kuti, “chokonzedwa bwino; chadongosolo; choyenerera.”
Mabaibulo ena amati, “zimene zinapita.”
Kapena kuti, “chifukwa limenelo ndi gawo lake.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ndipo amadya mnofu wake womwe.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “kupuma kodzaza dzanja limodzi.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ntchito yovuta yodzaza manja awiri.”
Kapena kuti, “phindu lalikulu.”
Kapena kuti, “mosavuta.”
Kapena kuti, “chifukwa cha zinthu zambiri zofunika kuzisamalira.”
Kapena kuti, “mthenga.”
Kapena kuti, “Pali tsoka lalikulu limene.”
Kapena kuti, “chifukwa cha ntchito.”
Kapena kuti, “Palinso tsoka lina lalikulu kwambiri.”
Kapena kuti, “Chifukwa limenelo ndi gawo lake.”
Kapena kuti, “kulandira gawo lake.”
Kapena kuti, “Pali tsoka limene.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “akupumula kwambiri.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “amadziwa kuyenda pamaso pa anthu amoyo.”
Kapena kuti, “kuposa kulakalaka ndi mtima.”
Kapena kuti, “kudziteteza pa mlandu wotsutsana.”
Mabaibulo ena amati, “Zinthu zikachuluka.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Dzina limaposa.”
Mabaibulo ena amati, “chifukwa kukwiya ndi chizindikiro cha anthu opusa.”
Kapena kuti, “amene ali ndi moyo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “akukutemberera.”
Kapena kuti, “wowongoka mtima.”
Kapena kuti, “njira yomasulirira zinthu.”
Kapena kuti, “mpweya; mphepo.”
Mabaibulo ena amati, “kuipa kwawoko sikudzawapulumutsa.”
Kapena kuti, “chokhumudwitsa.”
Kapena kuti, “ndione ntchito zonse.”
Mabaibulo ena amati, “anthu sagona tulo masana ndi usiku.”
Kapena kuti, “malipiro aliwonse.”
Zimenezi ndi zovala zowala zosonyeza kuti munthu akusangalala osati zovala za pamaliro.
Kapena kuti, “limeneli ndi gawo limene.”
Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mʼchilankhulo choyambirira, “uli kudzanja lake lamanja.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “uli kudzanja lake lamanzere.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mtima wake ulibe nzeru.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Mzimu; Mpweya.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “anthu olemera.”
Mabaibulo ena amati, “aziwaza mosamala.”
Mabaibulo ena amati, “Ngakhale pamene uli pabedi pako.”
Kapena kuti, “usafunire zoipa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “cholengedwa chouluka chamumlengalenga.”
Kapena kuti, “uthenga wako.”
Kapena kuti, “Tumiza.”
Kapena kuti, “adzakuimba mlandu.”
Kapena kuti, “masiku atsoka.”
Kapena kuti, “oyangʼanira.”
Mawu a mʼchilankhulo choyambirira amene amasuliridwa kuti “zakudya sizidzakoma,” akutanthauza kuti chipatso cha mtundu winawake chimene munthu amadya kuti zakudya ziyambirenso kumukomera, chaphulika.
Kapena kuti, “mphamvu ya moyo.”
Kapena kuti, “Nʼzopanda pake.”
Kapena kuti, “kuti aike mwandondomeko.”