Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • nwt 1 Peter 1:1-5:14
  • 1 Petulo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • 1 Petulo
  • Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
1 Petulo

KALATA YOYAMBA YA PETULO

1 Ine Petulo mtumwi+ wa Yesu Khristu, ndikulembera inu osankhidwa ndi Mulungu, amene muli alendo mʼdzikoli, omwe mwamwazikana ku Ponto, Galatiya, Kapadokiya,+ Asia ndi Bituniya. 2 Ndikulembera inu amene Mulungu Atate+ anadziwiratu za inu. Iye anakupatsani mzimu wake kuti mukhale oyera.+ Anachita zimenezi kuti mukhale omvera komanso kuti akuyeretseni ndi magazi a Yesu Khristu.+

Ndikupempha Mulungu kuti akusonyezeni chifundo chake chachikulu komanso kuti mukhale ndi mtendere.

3 Atamandike Mulungu wa Ambuye wathu Yesu Khristu, yemwenso ndi Atate wake. Mulungu anatisonyeza chifundo chachikulu pamene anachititsa kuti tibadwenso mwatsopano+ nʼkukhala ndi chiyembekezo chodalirika.+ Zimenezi zinatheka chifukwa cha kuukitsidwa kwa Yesu Khristu.+ 4 Anachititsa kuti tibadwenso mwatsopano kuti tikhale ndi cholowa chosawonongeka, chosadetsedwa ndiponso chosasuluka.+ Cholowa chimenechi anakusungirani kumwamba.+ 5 Anasungira inuyo amene Mulungu akukutetezani ndi mphamvu yake chifukwa muli ndi chikhulupiriro. Mulungu akukutetezani kuti mudzalandire chipulumutso, ndipo chipulumutso chimenechi chidzaonekera mu nthawi yamapeto. 6 Pa chifukwa chimenechi, mukusangalala kwambiri ngakhale kuti panopa nʼkoyenera kuti muvutike kwa kanthawi chifukwa cha mayesero osiyanasiyana+ amene mukukumana nawo. 7 Zimenezi zikukuchitikirani kuti chikhulupiriro chanu chidzachititse kuti mutamandidwe ndiponso kulandira ulemerero ndi ulemu, Yesu Khristu akadzaonekera.*+ Chikhulupiriro chanucho chayesedwa+ ndipo ndi chamtengo wapatali kuposa golide amene amawonongekabe ngakhale kuti anadutsa pamoto. 8 Ngakhale kuti Khristuyo simunamuonepo, mumamukonda. Ngakhale simukumuona panopa, mumamukhulupirira ndipo mukusangalala kwambiri ndi chimwemwe chodzaza tsaya, 9 popeza ndinu otsimikiza kuti chikhulupiriro chanu chidzachititsa kuti mupulumuke.+

10 Aneneri amene analosera za kukoma mtima kwakukulu kumene Mulungu anakusonyezani, anafufuza za chipulumutso chimenechi mwakhama ndiponso mosamala kwambiri.+ 11 Mzimu woyera unali utaneneratu kuti Khristu+ adzavutika ndipo kenako adzalandira ulemerero. Aneneri ankafufuza zizindikiro zimene mzimu woyera* unawasonyeza zokhudza nthawi yeniyeni komanso nyengo imene zimenezi zidzachitike.+ 12 Mulungu anauza aneneriwo kuti sankadzitumikira okha, koma ankatumikira inuyo. Tsopano zinthu zimenezi zaululidwa ndi anthu omwe akulengeza uthenga wabwino kwa inu mothandizidwa ndi mzimu woyera wochokera kumwamba.+ Angelo amafunitsitsa atamvetsa zinthu zimenezi.

13 Choncho konzekeretsani maganizo anu kuti mugwire ntchito mwamphamvu.+ Mukhalebe oganiza bwino+ ndipo muziyembekezera ndi mtima wonse kukoma mtima kwakukulu kumene adzakusonyezeni, Yesu Khristu akadzaonekera.* 14 Monga ana omvera, siyani kuchita zinthu motsatira zimene munkalakalaka musanadziwe Mulungu. 15 Koma mofanana ndi Woyera amene anakuitanani, inunso khalani oyera mʼmakhalidwe anu onse,+ 16 chifukwa Malemba amati: “Mukhale oyera, chifukwa ine ndine woyera.”+

17 Ndiponso ngati mukupempha zinthu kwa Atate, amene amaweruza mopanda tsankho+ mogwirizana ndi zimene aliyense amachita, muzichita zinthu zosonyeza kuti mumaopa Mulungu+ pamene mukukhala mʼdzikoli monga alendo. 18 Mukudziwa inu kuti zinthu zimene zinakumasulani*+ ku moyo wanu wopanda phindu umene munatengera kuchokera kwa makolo anu, sizinali zinthu zotha kuwonongeka monga siliva kapena golide. 19 Koma munamasulidwa ndi magazi amtengo wapatali+ a Khristu,+ omwe ndi ofanana ndi magazi a nkhosa yopanda chilema komanso yopanda mawanga.+ 20 Zoonadi, Mulungu anasankhiratu Khristu anthu asanayambe kuberekana padziko lapansi,+ koma anaonekera pa nthawi yamapeto chifukwa cha inuyo.+ 21 Kudzera mwa iye, mukukhulupirira Mulungu+ amene anamuukitsa kwa akufa+ ndi kumupatsa ulemerero,+ nʼcholinga choti chikhulupiriro ndiponso chiyembekezo chanu zikhale mwa Mulungu.

22 Popeza mwadziyeretsa pokhala omvera choonadi cha mʼMawu a Mulungu ndipo tsopano mumakonda abale mopanda chinyengo,+ muzikondana kwambiri kuchokera mumtima.+ 23 Inuyo mwabadwanso mwatsopano+ kudzera mʼmawu a Mulungu+ wamoyo ndi wamuyaya. Simunabadwe kuchokera mumbewu yoti ikhoza kuwonongeka, koma mumbewu yomwe singawonongeke.+ 24 Pakuti “anthu onse ali ngati udzu, ndipo ulemerero wawo wonse uli ngati duwa lakutchire. Udzu umafota ndipo duwa limathothoka, 25 koma mawu a Yehova* adzakhalapo mpaka kalekale.”+ “Mawu” amenewa ndi uthenga wabwino umene unalengezedwa kwa inu.+

2 Choncho siyani zoipa zonse,+ zachinyengo zonse, zachiphamaso, kaduka komanso miseche yamtundu uliwonse. 2 Koma monga ana ongobadwa kumene,+ muzilakalaka mkaka wosasungunula* umene uli mʼMawu a Mulungu. Mukamamwa mkaka umenewo, ukuthandizani kuti mukule nʼkukhala oyenera chipulumutso.+ 3 Zimenezi zingatheke ngati mutalawa nʼkuona kuti Ambuye ndi wokoma mtima.

4 Pamene mukubwera kwa Ambuye, amene ndi mwala wamoyo umene anthu anaukana,+ koma umene Mulungu anausankha, umenenso ndi wamtengo wapatali kwa Mulunguyo,+ 5 inunso monga miyala yamoyo mukumangidwa nʼkukhala nyumba yauzimu+ kuti mudzakhale ansembe oyera. Monga ansembe oyera muzidzapereka nsembe zauzimu+ zovomerezeka pamaso pa Mulungu kudzera mwa Yesu Khristu.+ 6 Paja Lemba limati: “Inetu ndikuika mwala wosankhidwa mwapadera mu Ziyoni. Umenewu ndi mwala wapakona ya maziko, womwe ndi wamtengo wapatali, ndipo aliyense wokhulupirira mwalawo sadzakhumudwa.”*+

7 Choncho iye ndi wamtengo wapatali kwa inu chifukwa mumamukhulupirira. Koma kwa amene samukhulupirira, “mwala umene omanga nyumba anaukana,+ wakhala mwala wapakona wofunika kwambiri.”+ 8 Wakhalanso “mwala wopunthwitsa ndi thanthwe lokhumudwitsa.”+ Anthu amenewa akupunthwa chifukwa samvera mawu, ndipo zimenezi nʼzimene zikuyenera kuwachitikira. 9 Koma inu ndi “fuko losankhidwa mwapadera, ansembe achifumu, mtundu woyera+ ndiponso anthu oti adzakhale chuma chapadera.+ Mwasankhidwa kuti mulengeze makhalidwe abwino kwambiri”+ a Mulungu amene anakuitanani kuti muchoke mumdima ndipo anakulandirani mʼkuwala kwake kodabwitsa.+ 10 Poyamba simunali anthu a Mulungu, koma tsopano ndinu anthu ake.+ Mulungu anali asanakuchitireni chifundo, koma tsopano wakuchitirani chifundo.+

11 Okondedwa, popeza ndinu alendo ndiponso anthu osakhalitsa mʼdzikoli,+ ndikukudandaulirani kuti muzipewa kulakalaka zinthu zoipa+ zomwe zili pankhondo yolimbana nanu.+ 12 Mukhale ndi khalidwe labwino pakati pa anthu amʼdzikoli,+ kuti akamakunenani kuti mumachita zoipa, aziona okha zochita zanu zabwino+ kuti kenako adzatamande Mulungu patsiku lake loyendera.

13 Muzichita zimene Ambuye amafuna pogonjera ulamuliro uliwonse wokhazikitsidwa ndi anthu.+ Muzigonjera mfumu+ chifukwa ili ndi udindo waukulu, 14 komanso nduna chifukwa zimatumidwa ndi mfumuyo kuti zipereke chilango kwa anthu amene achita zoipa ndiponso kuyamikira amene achita zabwino.+ 15 Mulungu amafuna kuti muzichita zabwino kuti muwatseke pakamwa anthu omwe amalankhula zopanda nzeru chifukwa cha umbuli.+ 16 Muli ndi ufulu,+ koma musamagwiritse ntchito ufulu wanuwo monga pobisalira pochita zoipa,+ koma muziugwiritsa ntchito potumikira Mulungu.+ 17 Muzilemekeza anthu amitundu yonse.+ Muzikonda gulu lonse la abale,+ muziopa Mulungu+ komanso muzilemekeza mfumu.+

18 Antchito azigonjera mabwana awo ndipo aziwalemekeza kwambiri.+ Asamachite zimenezi kwa mabwana abwino ndi ololera okha, koma ngakhalenso kwa ovuta kuwakondweretsa. 19 Ngati munthu akupirira pamene akuzunzidwa komanso kukumana ndi mavuto* chifukwa chomvera* Mulungu,+ Mulunguyo amasangalala naye. 20 Kodi kupirira pamene mukumenyedwa chifukwa choti mwachimwa kuli ndi phindu lanji?+ Koma Mulungu amasangalala mukamapirira mavuto chifukwa choti mukuchita zabwino.+

21 Ndipotu Mulungu anakuitanani kuti muyende mʼnjira imeneyi. Pajatu ngakhale Khristu anavutika chifukwa cha inu,+ ndipo anakusiyirani chitsanzo kuti mutsatire mapazi ake mosamala kwambiri.+ 22 Iye sanachite tchimo+ ndipo sananenepo mawu achinyengo.+ 23 Pamene anthu ankamunenera zachipongwe,+ sanabwezere zachipongwe.+ Pamene ankazunzidwa,+ sanaopseze anthu amene ankamuzunzawo. Koma anasiya zonse mʼmanja mwa Woweruza amene amaweruza+ mwachilungamo. 24 Iye ananyamula machimo athu+ mʼthupi lake pamene anamukhomerera pamtengo.+ Anachita zimenezi kuti tipulumutsidwe ku uchimo nʼkumachita zinthu zolungama. Ndipo “munachiritsidwa ndi mabala ake.”+ 25 Poyamba munali ngati nkhosa zosochera,+ koma tsopano mwabwerera kwa mʼbusa wanu+ ndi woyangʼanira miyoyo yanu.

3 Mofanana ndi zimenezi, inu akazi muzigonjera amuna anu+ kuti ngati safuna kumvera Mawu a Mulungu, akopeke ndi khalidwe lanu, osati ndi mawu anu+ 2 koma chifukwa choti aona khalidwe lanu labwino*+ komanso ulemu wanu waukulu. 3 Kudzikongoletsa kwanu kusakhale kwa kunja kokha monga kumanga tsitsi, kuvala zodzikongoletsera zagolide+ kapena zovala zapamwamba. 4 Koma kukhalenso kwa munthu wobisika mumtima, atavala zovala zosawonongeka, zomwe ndi mtima wodekha komanso wofatsa+ umene ndi wamtengo wapatali pamaso pa Mulungu. 5 Ndi mmenenso akazi okhulupirika akale, omwe ankayembekezera Mulungu, ankadzikongoletsera. Akazi amenewa ankagonjera amuna awo. 6 Mwachitsanzo, Sara ankamvera Abulahamu ndipo ankamutchula kuti “mbuyanga.”+ Tsopano inuyo mwakhala ana ake, ndipo mukhalabe ana ake mukapitiriza kuchita zabwino komanso ngati simukuopa chilichonse.+

7 Inunso amuna, pitirizani kukhala ndi akazi anu mowadziwa bwino. Muziwapatsa ulemu+ chifukwa akazi ali ngati chiwiya chosachedwa kusweka. Muzichita zimenezi kuti mapemphero anu asatsekerezedwe, chifukwa mudzalandira nawo limodzi moyo umene Mulungu adzakupatseni+ chifukwa cha kukoma mtima kwake kwakukulu.

8 Pomaliza, nonsenu mukhale amaganizo amodzi,+ muzimverana chisoni, muzikonda abale, mukhale ndi chifundo chachikulu+ ndiponso mukhale odzichepetsa.+ 9 Munthu akakuchitirani choipa musamabwezere ndi choipa,+ akakuchitirani chipongwe musamabwezere ndi chipongwe.+ Mʼmalomwake muziwachitira zabwino*+ chifukwa Mulungu anakusankhani kuti muzidalitsa ena kuti nayenso adzakudalitseni.

10 Munthu “amene amakonda moyo wake komanso amafuna kumakhala moyo wabwino, ayenera kusamala kuti asamalankhule zoipa ndi lilime lake+ ndiponso kuti asamalankhule zachinyengo ndi milomo yake. 11 Ayenera kusiya kuchita zoipa+ nʼkumachita zabwino.+ Ayeneranso kuyesetsa kumakhala mwamtendere ndi ena komanso kuulimbikitsa.+ 12 Maso a Yehova* ali pa olungama, ndipo makutu ake amamva mapemphero awo opembedzera,+ koma Yehova* amakwiyira anthu amene amachita zoipa.”+

13 Ndithudi, ndi ndani angakuchitireni zoipa mukamayesetsa kuchita zabwino?+ 14 Koma ngakhale mutavutika chifukwa chochita zinthu mwachilungamo, mumakhalabe osangalala.+ Musamaope zimene amaopa* ndipo musamade nazo nkhawa.+ 15 Koma muvomereze mumtima mwanu kuti Khristu ndi Ambuye ndiponso kuti ndi woyera. Nthawi zonse muzikhala okonzeka kuyankha aliyense amene wakufunsani za chiyembekezo chanu, koma muziwayankha mofatsa+ ndiponso mwaulemu kwambiri.+

16 Muzikhala ndi chikumbumtima chabwino,+ kuti kaya anthu akunenereni zoipa, amene akukunenerani zoipawo adzachite manyazi+ chifukwa cha khalidwe lanu labwino monga otsatira a Khristu.+ 17 Ndi bwino kuvutika chifukwa chochita zabwino,+ ngati Mulungu walola kuti zimenezo zichitike, kusiyana ndi kuvutika chifukwa chochita zoipa.+ 18 Pajatu ngakhale Khristu anafa kamodzi kokha kuti achotse uchimo.+ Munthu wolungamayo anafera anthu osalungama+ kuti akugwirizanitseni ndi Mulungu.+ Iye anaphedwa monga munthu,*+ koma anaukitsidwa monga mzimu.+ 19 Kenako anapita kukalengeza uthenga wachiweruzo* kwa mizimu imene inali mʼndende.+ 20 Mizimuyi sinamvere Mulungu pa nthawi imene ankaleza mtima mʼmasiku a Nowa.+ Pa nthawiyo, Nowa ankapanga chingalawa+ chomwe chinapulumutsa pamadzi anthu owerengeka, anthu* 8 okha basi.+

21 Tsopano ubatizo, womwe ukufanana ndi chingalawa, ukupulumutsanso inuyo (osati kungochotsa litsiro lamʼthupi, koma kupempha Mulungu kuti akupatseni chikumbumtima chabwino)+ chifukwa mumakhulupirira Yesu Khristu yemwe anaukitsidwa. 22 Iye anapita kumwamba ndipo ali kudzanja lamanja la Mulungu+ moti anamukweza kuti maulamuliro, mphamvu komanso angelo zikhale pansi pake.+

4 Popeza Khristu anavutika pa nthawi imene anali munthu,+ nanunso konzekerani pokhala ndi maganizo ofanana ndi amene Khristu anali nawo. Zili choncho chifukwa munthu amene akuvutika ndiye kuti anasiya kuchita machimo.+ 2 Anachita zimenezi kuti pa nthawi yonse imene ali moyo asamachite zofuna za anthu+ koma za Mulungu.+ 3 Mʼmbuyomu munkangokhalira kuchita zofuna za anthu amʼdzikoli.+ Pa nthawi imeneyo munkachita khalidwe lopanda manyazi,* munkalakalaka zoipa, munkamwa vinyo mopitirira muyezo, munkakonda maphwando oipa,* munkapanga mipikisano yomwa mowa komanso munkapembedza mafano, komwe kunali kuphwanya malamulo.+ 4 Chifukwa choti munasiya kuthamanga nawo limodzi mʼchithaphwi cha* makhalidwe oipa, anthu amʼdzikoli sakumvetsa, choncho amakunyozani.+ 5 Koma anthu amenewa adzayankha mlandu kwa Khristu yemwe adzaweruze amoyo ndi akufa omwe.+ 6 Nʼchifukwa chake uthenga wabwino unalengezedwanso kwa akufa,+ kuti ngakhale akuweruzidwa malinga ndi mmene akuonekera,* mogwirizana ndi kuona kwa anthu, akhale ndi moyo mwa mzimu mogwirizana ndi kuona kwa Mulungu.

7 Koma mapeto a zinthu zonse ayandikira. Choncho khalani oganiza bwino,+ ndipo khalani maso kuti musanyalanyaze kupemphera.+ 8 Koposa zonse, muzikondana kwambiri+ chifukwa chikondi chimakwirira machimo ochuluka.+ 9 Muzicherezana popanda kudandaula.+ 10 Aliyense wa inu analandira mphatso, choncho muzigwiritsa ntchito mphatso zanuzo potumikirana. Muzichita zimenezi monga atumiki amene amathandiza ena kuti apindule ndi kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu, kumene amakusonyeza mʼnjira zosiyanasiyana.+ 11 Ngati wina ali ndi mphatso ya kulankhula, azilankhula mogwirizana ndi mawu opatulika a Mulungu. Ngati wina akutumikira ena, aziwatumikira modalira mphamvu imene Mulungu amapereka.+ Azichita zimenezi kuti Mulungu alemekezeke mʼzinthu zonse+ kudzera mwa Yesu Khristu. Ulemerero ndi mphamvu ndi zake mpaka muyaya. Ame.

12 Okondedwa, musadabwe ndi mayesero oyaka moto amene mukukumana nawo+ ngati kuti mukukumana ndi chinachake chachilendo. 13 Koma muzisangalala+ chifukwa mukukumana ndi mayesero ofanana ndi amene Khristu anakumana nawo+ kuti mudzasangalalenso kwambiri pa nthawi imene ulemerero wake udzaonekere.*+ 14 Ndinu osangalala*+ ngati anthu akukunyozani chifukwa cha dzina la Khristu chifukwa zimenezi zikusonyeza kuti mzimu woyera wa Mulungu komanso ulemerero wake zili pa inu.

15 Koma sindikufuna kuti wina wa inu azivutika chifukwa choti wayamba kuba, kupha anthu, kuchita zoipa kapena chifukwa choti akulowerera nkhani za eni.+ 16 Koma ngati wina akuvutika chifukwa chokhala Mkhristu, asachite manyazi,+ koma apitirize kulemekeza Mulungu kwinaku akudziwikabe monga Mkhristu. 17 Inoyo ndi nthawi imene Mulungu anasankhiratu kuti apereke chiweruzo, ndipo chiyambira panyumba yake.+ Komano ngati chikuyambira pa ifeyo,+ ndiye anthu osamvera uthenga wabwino wa Mulungu zidzawathera bwanji?+ 18 “Ndipo ngati munthu wolungama angadzapulumuke movutikira, kodi chidzachitike nʼchiyani kwa munthu wosaopa Mulungu komanso wochimwa?”+ 19 Choncho amene akuvutika chifukwa choti akuchita zimene Mulungu amafuna, apereke moyo wawo kwa Mlengi wathu amene ndi wokhulupirika nʼkumapitiriza kuchita zabwino.+

5 Choncho, ine monga mkulu mnzanu, amene ndinaona mmene Khristu anavutikira komanso ndikuyembekezera kudzalandira nawo ulemerero umene udzaonekere,+ ndikupempha akulu amene ali pakati panu kuti: 2 Wetani gulu la nkhosa za Mulungu+ zomwe zili mʼmanja mwanu. Monga oyangʼanira, muzigwira ntchito yanu, osati mokakamizika koma mofunitsitsa monga atumiki a Mulungu.+ Muziigwira ndi mtima wonse, osati chifukwa chofuna kupindulapo kenakake.+ 3 Musamachite zinthu ngati mafumu pakati pa anthu a Mulungu,*+ koma muzipereka chitsanzo chabwino kwa gulu la nkhosa.+ 4 Ndipo mʼbusa wamkulu+ akadzaonekera, mudzalandira mphoto* yosawonongeka yomwe ndi yaulemerero.+

5 Chimodzimodzinso inu achinyamata, muzigonjera amuna achikulire.*+ Komanso nonsenu muzichitirana zinthu modzichepetsa* chifukwa Mulungu sasangalala ndi anthu odzikuza. Koma anthu odzichepetsa amawasonyeza kukoma mtima kwake kwakukulu.+

6 Choncho dzichepetseni pamaso pa Mulungu wathu wamphamvu* kuti adzakukwezeni nthawi yake ikadzakwana.+ 7 Muzichita zimenezi pamene mukumutulira nkhawa zanu zonse,+ chifukwa amakufunirani zabwino.+ 8 Khalanibe oganiza bwino ndipo khalani tcheru+ chifukwa mdani wanu Mdyerekezi akuyendayenda ngati mkango wobangula, kuti ameze winawake.*+ 9 Choncho mukhale ndi chikhulupiriro cholimba ndipo mulimbane naye,+ podziwa kuti abale anu padziko lonse akukumananso ndi mavuto ngati omwewo.+ 10 Mukavutika kwa nthawi yochepa, Mulungu yemwe amasonyeza kukoma mtima konse kwakukulu, amenenso anakuitanani kuti mukhale ogwirizana ndi Khristu komanso kuti mulandire ulemerero wosatha,+ adzamalizitsa kukuphunzitsani. Iye adzakupatsani mphamvu,+ adzakuthandizani kuti mukhalebe okhulupirika+ komanso adzakulimbitsani. 11 Mphamvu ndi zake mpaka muyaya. Ame.

12 Ndakulemberani kalata yachiduleyi kudzera mwa Silivano,*+ mʼbale amene ndikumuona kuti ndi wokhulupirika. Ndakulemberani zimenezi kuti ndikulimbikitseni ndi kukutsimikizirani kuti kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu nʼkumeneku, ndipo mukugwire mwamphamvu. 13 Mayi* amene ali ku Babulo, yemwe Mulungu anamusankha mwapadera ngati inuyo, komanso mwana wanga Maliko,+ akupereka moni. 14 Patsanani moni mwachikondi.*

Nonse amene muli ogwirizana ndi Khristu, mukhale ndi mtendere.

Mʼchilankhulo choyambirira, “akadzaululika.”

Kapena kuti, “mzimu woyera umene unali mwa iwo.”

Onani mawu amʼmunsi pavesi 7.

Mʼchilankhulo choyambirira, “zinakuwombolani.”

Onani Zakumapeto A5.

Kapena kuti, “wosasukuluka.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “sadzachititsidwa manyazi.”

Kapena kuti, “kumva chisoni; kumva kupweteka.”

Kapena kuti, “chifukwa cha chikumbumtima chake.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “loyera.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Mʼmalomwake muziwadalitsa.”

Onani Zakumapeto A5.

Onani Zakumapeto A5.

Mabaibulo ena amati, “Musamaope akamakuopsezani.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Iye anaphedwa mʼthupi.”

Kapena kuti, “Kenako anapita kukalalikira.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “miyoyo.”

Kapena kuti, “munkachita makhalidwe opanda manyazi.” Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Kapena kuti, “maphwando aphokoso.”

Kapena kuti, “mʼmatope onyansa a.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “akuweruzidwa mwa thupi.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “udzaululike.”

Kapena kuti, “Ndinu odala.”

Kapena kuti, “pakati pa anthu omwe ndi cholowa cha Mulungu.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “chipewa chachifumu chosawonongeka.”

Kapena kuti, “akulu.”

Kapena kuti, “muvale kudzichepetsa.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “dzichepetseni pansi pa dzanja lamphamvu la Mulungu.”

Kapena kuti, “ngati mkango wobangula umene ukufunafuna winawake woti umumeze.”

Yemwe amadziwikanso kuti Sila.

Mawu akuti “mayi,” nʼkutheka kuti akutanthauza mpingo.

Mʼchilankhulo choyambirira, “popsopsonana mwachikondi.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena