Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • nwt Galatians 1:1-6:18
  • Agalatiya

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Agalatiya
  • Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Agalatiya

KALATA YOPITA KWA AGALATIYA

1 Ine Paulo, ndine mtumwi, osati wochokera kwa anthu kapena woikidwa kudzera mwa munthu, koma kudzera mwa Yesu Khristu+ komanso kudzera mwa Mulungu Atate+ amene anamuukitsa kwa akufa. 2 Ineyo limodzi ndi abale onse amene ali ndi ine tikupereka moni ku mipingo ya ku Galatiya:

3 Kukoma mtima kwakukulu ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate wathu ndi Ambuye Yesu Khristu, zikhale nanu. 4 Iye anadzipereka chifukwa cha machimo athu,+ kuti atipulumutse ku dziko loipali,*+ mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu amene ndi Atate wathu.+ 5 Ulemerero ukhale kwa Mulunguyo mpaka muyaya. Ame.

6 Ine ndikudabwa kuti mwapatuka mwamsanga* kuchoka kwa Mulungu amene anakuitanani kudzera mu kukoma mtima kwakukulu kwa Khristu ndipo mwayamba kumvetsera uthenga wabwino wamtundu wina.+ 7 Koma umenewo sikuti ndi uthenga wabwino, kungoti pali anthu ena amene akukusokonezani+ ndipo akufuna kupotoza uthenga wabwino wonena za Khristu. 8 Komabe, ngati ifeyo kapena mngelo wochokera kumwamba angalengeze nkhani ina kwa inu nʼkumanena kuti akulengeza uthenga wabwino, koma nkhaniyo nʼkukhala yosiyana ndi uthenga wabwino umene tinaulengeza kwa inu, ameneyo akhale wotembereredwa. 9 Monga mmene tanenera kale, ndikunenanso kuti, Aliyense amene akulengeza nkhani ina kwa inu nʼkumati ndi uthenga wabwino, koma yosiyana ndi imene munalandira, ameneyo akhale wotembereredwa.

10 Ndiye kodi panopa ndikufuna kuti ndizikondedwa ndi anthu kapena Mulungu? Kapena kodi ndikungofuna kusangalatsa anthu? Ndikanakhala kuti ndikusangalatsabe anthu, sindikanakhala kapolo wa Khristu. 11 Chifukwa ndikufuna kuti mudziwe abale, kuti uthenga wabwino umene ndinalengeza kwa inu sunachokere kwa anthu.+ 12 Uthengawu sindinaulandire kwa munthu ndipo sindinachite kuphunzitsidwa, koma Yesu Khristu ndi amene anandiululira uthenga umenewu.

13 Munamva ndithu zimene ndinkachita ndili mʼChiyuda,+ kuti ndinkazunza kwambiri mpingo wa Mulungu ndipo ndinapitiriza kuuwononga.+ 14 Ndinkachita bwino kwambiri mʼchipembedzo cha Chiyuda kuposa anzanga ambiri a fuko langa, omwe anali amsinkhu wanga, chifukwa ndinali wodzipereka kwambiri pa miyambo ya makolo anga.+ 15 Koma pamene Mulungu, amene anandichititsa kuti ndibadwe komanso kundiitana kudzera mu kukoma mtima kwake kwakukulu,+ anaona kuti nʼzabwino kuti 16 aulule za Mwana wake kudzera mwa ine, nʼcholinga choti ndilengeze kwa anthu a mitundu ina+ uthenga wabwino wonena za iye, sindinapite kukakambirana ndi munthu aliyense* nthawi yomweyo. 17 Sindinapitenso ku Yerusalemu kwa amene anakhala atumwi ine ndisanakhale, koma ndinapita ku Arabiya, kenako ndinabwereranso ku Damasiko.+

18 Ndiye pambuyo pa zaka zitatu, ndinapita ku Yerusalemu+ kukacheza kwa Kefa*+ ndipo ndinakhala naye masiku 15. 19 Koma atumwi ena onse sindinawaone kupatulapo Yakobo,+ mchimwene wa Ambuye. 20 Zimene ndikukulemberanizi, ndikukutsimikizirani pamaso pa Mulungu kuti sindikunama.

21 Kenako ndinalowa mʼmadera a Siriya ndi Kilikiya.+ 22 Koma anthu a mʼmipingo ya ku Yudeya yomwe inali yogwirizana ndi Khristu, sankandidziwa bwinobwino. 23 Iwo ankangomva kuti: “Munthu amene kale ankatizunza uja+ komanso kuwononga mipingo* tsopano akulengeza uthenga wabwino.”+ 24 Choncho anthuwo anayamba kulemekeza Mulungu chifukwa cha ine.

2 Ndiyeno patapita zaka 14, ndinapitanso ku Yerusalemu ndi Baranaba+ ndipo ndinatenganso Tito.+ 2 Ndinapita kumeneko chifukwa ndinauzidwa mʼmasomphenya kuti ndipiteko. Ndipo abale ndinawafotokozera uthenga wabwino umene ndikuulalikira kwa anthu a mitundu ina. Koma ndinachita zimenezi mwachinsinsi kwa abale odalirika okha pofuna kutsimikizira kuti utumiki wanga sukupita pachabe. 3 Ndipo ngakhale kuti Tito,+ amene ndinali naye limodzi anali Mgiriki, sanakakamizidwe kuti adulidwe.+ 4 Koma nkhani imeneyi inayambika chifukwa cha abale achinyengo amene analowa pakati pathu mwakachetechete+ ndiponso mozemba ngati akazitape, nʼcholinga choti asokoneze ufulu+ umene tikusangalala nawo mogwirizana ndi Khristu Yesu, nʼkutisandutsa akapolo.+ 5 Anthu amenewa sitinawagonjere,+ ngakhale kwa kanthawi kochepa,* kuti inuyo mupitirize kukhala ndi choonadi cha uthenga wabwino.

6 Koma kunena za anthu amene ankaoneka ngati apadera aja,+ kaya anali otani, zilibe kanthu kwa ine, chifukwa Mulungu sayangʼana maonekedwe a munthu, amuna odalirika amenewo sanandiphunzitse chilichonse chatsopano. 7 Koma ataona kuti ndapatsidwa ntchito yolalikira uthenga wabwino kwa anthu osadulidwa,+ mofanana ndi Petulo amene anapatsidwa ntchito yoti akalalikire uthenga wabwino kwa anthu odulidwa, 8 pajatu amene anapatsa Petulo mphamvu kuti akhale mtumwi kwa anthu odulidwa ndi amene anandipatsanso ine mphamvu kuti ndikhale mtumwi kwa anthu a mitundu ina.+ 9 Iwo atazindikira kukoma mtima kwakukulu kumene ndinapatsidwa,+ Yakobo,+ Kefa* ndi Yohane, amene anali ngati zipilala, anagwira chanza ineyo ndi Baranaba+ posonyeza kuti agwirizana ndi zoti ife tipite kwa anthu a mitundu ina ndipo iwo apite kwa anthu odulidwa. 10 Iwo anangotipempha kuti tizikumbukira osauka ndipo ndayesetsa moona mtima kuchita zimenezi.+

11 Koma Kefa*+ atabwera ku Antiokeya,+ ndinamudzudzula* pamasomʼpamaso chifukwa zinali zoonekeratu kuti anachita zolakwika. 12 Chifukwa asanafike anthu ena ochokera kwa Yakobo,+ iye ankadya limodzi ndi anthu a mitundu ina.+ Koma anthuwo atafika, iye anasiya kuchita zimenezi ndipo anadzipatula, chifukwa ankaopa anthu odulidwawo.+ 13 Ayuda enawonso anagwirizana naye pochita zachiphamaso* zimenezi. Ngakhale Baranaba nayenso anachita nawo zachiphamasozi.* 14 Koma nditaona kuti sankachita zinthu mogwirizana ndi choonadi cha uthenga wabwino,+ ndinauza Kefa* pamaso pa onse kuti: “Ngati iweyo, ngakhale kuti ndiwe Myuda, ukukhala ngati anthu a mitundu ina, osati ngati Ayuda, nʼchifukwa chiyani ukufuna kuchititsa anthu a mitundu ina kuti azitsatira chikhalidwe cha Ayuda?”+

15 Ifeyo amene ndi a mtundu wa Chiyuda, osati ochimwa ochokera mwa anthu a mitundu ina, 16 tikudziwa kuti munthu amaonedwa kuti ndi wolungama, osati chifukwa chotsatira chilamulo, koma chifukwa chokhulupirira+ Yesu Khristu basi.+ Choncho ifeyo tikukhulupirira Khristu Yesu kuti tionedwe olungama chifukwa chokhulupirira Khristu, osati chifukwa chotsatira chilamulo. Tachita zimenezi chifukwa palibe munthu amene amaonedwa wolungama chifukwa chotsatira chilamulo.+ 17 Ndiye ngati ife tapezekanso kuti ndife ochimwa pamene tikuyesetsa kuti tiyesedwe olungama kudzera mwa Khristu, kodi ndiye kuti Khristu wakhala mtumiki wa uchimo? Ayi ndithu. 18 Ngati ndikumanganso zinthu zimene ndinagwetsa, ndiye kuti ndikusonyeza kuti ndine wophwanya malamulo. 19 Chifukwa choti ndinkatsatira chilamulo, ndinafa ku chilamulo+ kuti ndikhale moyo nʼkumatumikira Mulungu. 20 Ndinakhomereredwa pamtengo limodzi ndi Khristu.+ Si inenso amene ndikukhala ndi moyo,+ koma Khristu ndi amene ali ndi moyo ndipo ndi wogwirizana ndi ine. Zoonadi, moyo umene ndikukhala tsopano, ndikukhala mokhulupirira Mwana wa Mulungu,+ amene anandikonda nʼkudzipereka yekha chifukwa cha ine.+ 21 Sindikukana* kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu,+ chifukwa ngati munthu amakhala wolungama potsatira chilamulo, ndiye kuti Khristu anangofa pachabe.+

3 Agalatiya opusa inu! Kodi ndi ndani amene anakupusitsani,+ inu amene munakhala ngati mwaona Yesu Khristu atakhomereredwa pamtengo?+ 2 Ndikufuna ndikufunseni* chinthu chimodzi: Kodi munalandira mzimu chifukwa cha ntchito za chilamulo kapena chifukwa chokhulupirira zimene munamva?+ 3 Kodi ndinu opusa chonchi? Munayamba ndi kudalira mzimu, kodi tsopano mukufuna kumaliza ndi kudalira nzeru za anthu omwe si angwiro?+ 4 Kodi kuvutika konse kuja kunangopita pachabe? Ndikukhulupirira kuti sikunapite pachabe. 5 Ndiye kodi amene amakupatsani mzimu ndi kuchita zinthu zamphamvu pakati panu,+ amachita zimenezi chifukwa chakuti inuyo mukuchita ntchito za chilamulo kapena chifukwa chakuti munakhulupirira uthenga wabwino umene munamva? 6 Taganizirani za Abulahamu. Iye “anakhulupirira zimene Yehova* anamuuza ndipo ankaonedwa kuti ndi wolungama.”+

7 Ndithudi mukudziwa kuti amene amakhalabe ndi chikhulupiriro ndi amene ali ana a Abulahamu.+ 8 Kale malemba ananeneratu kuti Mulungu adzaona anthu a mitundu ina kuti ndi olungama chifukwa cha chikhulupiriro. Choncho analengezeratu uthenga wabwino kwa Abulahamu wakuti: “Kudzera mwa iwe, mitundu yonse idzadalitsidwa.”+ 9 Choncho amene ali ndi chikhulupiriro champhamvu akudalitsidwa limodzi ndi Abulahamu, yemwe anali ndi chikhulupiriro.+

10 Onse amene amadalira ntchito za chilamulo ndi otembereredwa, chifukwa Malemba amati: “Munthu aliyense amene sakupitiriza kutsatira zinthu zonse zimene zinalembedwa mumpukutu wa Chilamulo ndi wotembereredwa.”+ 11 Komanso, nʼzodziwikiratu kuti palibe munthu amene Mulungu angamuone kuti ndi wolungama chifukwa cha chilamulo,+ popeza “wolungama adzakhala ndi moyo chifukwa cha chikhulupiriro chake.”+ 12 Tsopano Chilamulo sichidalira chikhulupiriro. Koma “aliyense amene akuchita za mʼChilamulo adzakhala ndi moyo chifukwa cha chilamulocho.”+ 13 Khristu anatigula+ nʼkutimasula+ ku temberero la Chilamulo. Anachita zimenezi pokhala temberero mʼmalo mwa ife, chifukwa Malemba amati: “Munthu aliyense wopachikidwa pamtengo ndi wotembereredwa.”+ 14 Cholinga chake chinali chakuti kudzera mwa Khristu Yesu, mitundu ya anthu ipeze madalitso amene Abulahamu analonjezedwa,+ kuti tidzalandire mzimu wolonjezedwawo+ chifukwa cha chikhulupiriro chathu.

15 Abale, ndipereke fanizo mogwirizana ndi zimene zimachitika pakati pa anthu: Pangano likakhazikitsidwa, ngakhale kuti ndi pangano la anthu, palibe amene angalithetse kapena kuwonjezerapo mfundo zina. 16 Tsopano malonjezo anaperekedwa kwa Abulahamu ndi kwa mbadwa yake.*+ Malemba sanena kuti: “Kwa mbadwa zako,”* ngati kuti mbadwazo nʼzambiri. Koma akunena kuti, “kwa mbadwa yako,”* kutanthauza kuti ndi imodzi, amene ndi Khristu.+ 17 Komanso ineyo ndikuti: Choyamba, Mulungu anachita pangano ndi Abulahamu ndipo patapita zaka 430+ anapereka Chilamulo kwa anthu ake. Koma Chilamulocho sichinathetse pangano ndi lonjezo limene Mulungu anachita ndi Abulahamu, kuti lonjezolo lisagwirenso ntchito. 18 Chifukwa ngati Mulungu amapereka cholowa kudzera mʼchilamulo ndiye kuti sichidaliranso lonjezo. Koma mokoma mtima Mulungu wachipereka kwa Abulahamu kudzera mu lonjezo.+

19 Ndiye nʼchifukwa chiyani Chilamulo chinaperekedwa? Anatipatsa Chilamulochi kuti machimo aonekere,+ mpaka mbadwa* imene inapatsidwa lonjezolo itafika.+ Angelo anapereka Chilamulocho+ kudzera mʼdzanja la mkhalapakati.+ 20 Ngati pangano likukhudza munthu mmodzi sipakhala mkhalapakati. Ndi mmenenso zinalili ndi Mulungu, anali yekha pamene anapereka lonjezoli. 21 Ndiye kodi Chilamulo chimatsutsa malonjezo a Mulungu? Ayi ndithu. Chifukwa pakanaperekedwa lamulo lopatsa moyo, bwenzi tikuonedwa kuti ndife olungama chifukwa chotsatira chilamulo. 22 Koma Malemba amasonyeza kuti anthu akulamuliridwa ndi uchimo, kuti lonjezo limene limakhalapo chifukwa chokhulupirira Yesu Khristu, liperekedwe kwa anthu amene akumukhulupirira.

23 Komabe chikhulupirirocho chisanafike, chilamulo ndi chimene chinkatiyangʼanira ndipo chinatiika mu ukapolo. Pa nthawi imeneyo, tinkayembekezera chikhulupiriro chimene chinali chitatsala pangʼono kuonekera.+ 24 Choncho Chilamulo chinakhala wotiyangʼanira* amene anatitsogolera kwa Khristu,+ kuti tionedwe kuti ndife anthu olungama chifukwa cha chikhulupiriro.+ 25 Koma popeza chikhulupirirocho tsopano chafika,+ sitilinso pansi pa wotiyangʼanirayo.*+

26 Ndipotu nonsenu ndinu ana a Mulungu+ chifukwa mumakhulupirira Khristu Yesu.+ 27 Chifukwa nonsenu amene munabatizidwa ndipo ndinu ogwirizana ndi Khristu mwakhala ndi makhalidwe ngati a Khristu.+ 28 Palibe Myuda kapena Mgiriki,+ palibe kapolo kapena mfulu,+ palibenso mwamuna kapena mkazi+ chifukwa nonsenu ndinu amodzi mwa Khristu Yesu.+ 29 Ndiponso ngati muli ophunzira a Khristu, ndinudi mbadwa* za Abulahamu,+ olandira cholowa+ mogwirizana ndi lonjezolo.+

4 Tsopano ndikunena kuti, wolandira cholowa akakhala mwana wamngʼono, iye sasiyana ndi kapolo, ngakhale kuti ndi mwiniwake wa zinthu zonse. 2 Koma amakhalabe pansi pa amuna oyangʼanira ana ndiponso anthu oyangʼanira zinthu za mbuye wawo, mpaka tsiku limene bambo ake anaikiratu. 3 Nʼchimodzimodzinso ifeyo. Pamene tinali ana, tinali akapolo chifukwa tinkayendera mfundo zimene anthu amʼdzikoli amayendera.*+ 4 Koma nthawi itakwana, Mulungu anatumiza Mwana wake, amene anabadwa kudzera mwa mkazi+ ndipo anakhala pansi pa chilamulo.+ 5 Anachita zimenezi kuti apereke malipiro omasulira anthu amene anali pansi pa chilamulo+ nʼcholinga choti Mulungu atitenge nʼkukhala ana ake.+

6 Tsopano popeza ndinu ana ake, Mulunguyo watumiza mzimu+ wa Mwana wake mʼmitima yathu+ ndipo mzimuwo ukufuula kuti: “Abba,* Atate!”+ 7 Choncho aliyense wa inu si kapolo, koma mwana. Ndipo ngati ndiwe mwana, ndiye kuti ndiwenso wolandira cholowa chimene Mulungu adzakupatse.+

8 Ngakhale zili choncho, pamene simunkadziwa Mulungu, munali akapolo a zinthu zimene kwenikweni si milungu. 9 Koma panopa mwadziwa Mulungu, kapena tinene kuti tsopano mwadziwidwa ndi Mulungu. Ndiye mukubwereranso bwanji ku mfundo zimene anthu amʼdzikoli amayendera, zomwe ndi zosathandiza+ ndiponso zopanda pake, nʼkumafuna kukhalanso akapolo ake?+ 10 Mukuchita zikondwerero pa masiku, miyezi,+ nyengo ndi zaka zimene mukuganiza kuti nʼzapadera. 11 Ndikuda nkhawa kuti mwina ntchito imene ndinagwira pokuthandizani yangopita pachabe.

12 Ndikukupemphani abale anga kuti mukhale ngati ine chifukwa inenso poyamba ndinali ngati inuyo.+ Simunandilakwire ayi. 13 Koma mukudziwa kuti ndinapeza mwayi wolengeza uthenga wabwino koyamba kwa inu chifukwa chakuti ndinkadwala. 14 Ndipo ngakhale kuti matenda anga anali mayesero kwa inu, simunanyansidwe kapena kuipidwa nane.* Koma munandilandira ngati mngelo wa Mulungu kapena ngati Khristu Yesu. 15 Ndiye chimwemwe chimene munali nacho poyamba chija chili kuti? Chifukwa ndikutsimikiza kuti, ngati zikanakhala zotheka, mukanatha kukolowola maso anu nʼkundipatsa.+ 16 Kodi pano ndakhala mdani wanu chifukwa ndakuuzani zoona? 17 Anthu ena akuyesetsa kwambiri kuti akukopeni nʼcholinga choti muziwatsatira. Iwo sakuchita zimenezi ndi zolinga zabwino, koma akufuna kuti akuchotseni kwa ine, kuti inuyo muziwatsatira. 18 Zili bwino ngati munthu akukusonyezani chidwi kwambiri ndi zolinga zabwino osati pokhapokha pamene ndili limodzi ndi inu, koma nthawi zonse. 19 Inu ana anga,+ ndayambanso kumva kupweteka chifukwa cha inu ngati mayi amene watsala pangʼono kubereka. Ndipitiriza kumva kupweteka kumeneku mpaka mudzayambe kusonyeza makhalidwe a Khristu. 20 Panopa ndikanakonda ndikanakhala nanu limodzi kuti ndikulankhuleni mwa njira ina, chifukwa mwandithetsa nzeru.

21 Tandiuzani, inu amene mukufuna kuti muzitsatira chilamulo, Kodi simukumva zimene Chilamulocho chikunena? 22 Mwachitsanzo, Malemba amanena kuti Abulahamu anabereka ana aamuna awiri, wina kwa kapolo wamkazi+ ndipo wina kwa mkazi amene anali mfulu.+ 23 Koma mwana amene anabadwa kwa kapolo wamkazi uja anabadwa monga mmene ana onse amabadwira,+ pamene mwana winayo amene anabadwa kwa mkazi yemwe anali mfulu anabadwa kudzera mu lonjezo.+ 24 Zinthu zimenezi zili ndi tanthauzo lophiphiritsira, chifukwa azimayi amenewa akuimira mapangano awiri. Loyamba ndi pangano la paphiri la Sinai,+ limene limabereka ana oti akhale akapolo. Pangano limenelo ndi Hagara uja. 25 Tsopano, Hagara ameneyu akutanthauza Sinai,+ phiri lomwe lili ku Arabiya, ndipo masiku ano akufanana ndi Yerusalemu, chifukwa ali mu ukapolo pamodzi ndi ana ake. 26 Koma Yerusalemu wamʼmwamba ndi mfulu ndipo ndi mayi athu.

27 Chifukwa Malemba amati: “Sangalala, mkazi wosabereka iwe amene sunaberekepo mwana. Fuula mosangalala, iwe mkazi amene sunamvepo zowawa za pobereka, chifukwa ana a mkazi wosiyidwa ndi ambiri kuposa ana a mkazi amene ali ndi mwamuna.”+ 28 Tsopano inuyo abale, ndinu ana amene munabadwa chifukwa cha lonjezo la Mulungu mofanana ndi Isaki.+ 29 Koma mofanana ndi mmene zinalili pa nthawiyo, kuti amene anabadwa ngati mmene ana onse amabadwira anayamba kuzunza amene anabadwa kudzera mwa mzimu,+ ndi mmenenso zilili masiku ano.+ 30 Ngakhale zili choncho, kodi Malemba amati chiyani? “Thamangitsani kapolo wamkaziyu pamodzi ndi mwana wakeyu pano, chifukwa mwana wa kapolo ameneyu sadzakhala wolandira cholowa pamodzi ndi mwana wa mkazi amene ndi mfulu.”+ 31 Choncho abale, ife ndife ana a mkazi yemwe ndi mfulu, osati a kapolo wamkazi.

5 Khristu anatimasula kuti tikhale ndi ufulu umenewu. Choncho khalani olimba+ ndipo musalole kuti mumangidwenso mugoli la ukapolo.+

2 Tamverani! Ine Paulo, ndikukuuzani kuti mukadulidwa, zimene Khristu anachita sizidzakhala zaphindu kwa inu.+ 3 Kachiwirinso ndikukumbutsa munthu aliyense amene akudulidwa, kuti afunikanso kutsatira zonse za mʼChilamulo.+ 4 Inu amene mukufuna kuti muzionedwa kuti ndinu olungama chifukwa chotsatira chilamulo,+ mwadzilekanitsa ndi Khristu. Ndipo mwachititsa kuti musadzalandirenso kukoma mtima kwake kwakukulu. 5 Koma kudzera mwa mzimu, ife tikuyembekezera mwachidwi zimene zidzatichitikire chifukwa choonedwa kuti ndife olungama, chifukwa cha chikhulupiriro. 6 Chifukwa ngati munthu ali wogwirizana ndi Khristu Yesu, kudulidwa kapena kusadulidwa kumakhala kopanda ntchito.+ Koma chofunika kwambiri nʼkukhala ndi chikhulupiriro chimene chimaonekera posonyeza chikondi.

7 Munkathamanga bwino.+ Anakusokonezani ndi ndani kuti musapitirize kumvera choonadi? 8 Zimene anthu omwe anakusokonezaniwo ankaphunzitsa sizinachokere kwa Mulungu amene anakuitanani. 9 Zofufumitsa zochepa zimafufumitsa mtanda wonse.+ 10 Ndikukhulupirira kuti inu amene muli ogwirizana ndi Ambuye,+ simudzasintha maganizo. Koma munthu amene amakuvutitsaniyo+ kaya akhale ndani, adzalandira chiweruzo chomuyenerera. 11 Kunena za ine abale, ngati ndikulalikirabe kuti anthu azidulidwa, nʼchifukwa chiyani ndikuzunzidwabe? Zikanakhala choncho, ndiye kuti zimene ndimaphunzitsa zokhudza imfa ya Yesu pamtengo wozunzikirapo,*+ sizikanakhumudwitsanso anthu. 12 Ndikanakonda kuti anthu amene akufuna kukupotozani maganizowo, adzifule okha.*

13 Abale, munaitanidwa kuti mukhale aufulu. Koma musagwiritse ntchito ufulu umenewu ngati mwayi woti muzichita zimene thupi lomwe si langwiro limalakalaka.+ Mʼmalomwake muzilola kuti chikondi chizikulimbikitsani kutumikirana.+ 14 Chifukwa Chilamulo chonse chagona* mulamulo limodzi lakuti: “Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.”+ 15 Koma mukapitiriza kulumana komanso kudyana nokhanokha,+ samalani kuti musawonongane.+

16 Mʼmalomwake ndikuti, Pitirizani kuyenda motsogoleredwa ndi mzimu,+ ndipo simudzachita zimene thupi lomwe si langwiro likulakalaka ngakhale pangʼono.+ 17 Chifukwa zimene thupi limalakalaka zimalimbana ndi mzimu ndipo mzimu nawonso umalimbana ndi thupi. Zinthu ziwiri zimenezi zimatsutsana kuti musachite zinthu zimene mumafuna kuchita.+ 18 Komanso ngati mukutsogoleredwa ndi mzimu, simuli pansi pa chilamulo.

19 Tsopano ntchito za thupi lochimwali zimaonekera mosavuta. Ntchito zimenezi ndi chiwerewere,*+ khalidwe limene limadetsa munthu, khalidwe lopanda manyazi,*+ 20 kulambira mafano, kukhulupirira mizimu,*+ chidani, ndewu, nsanje, kupsa mtima, mikangano, kugawikana, magulu ampatuko, 21 kaduka, kumwa mwauchidakwa,*+ maphwando oipa,* ndi zina zotero.+ Abale, mogwirizana ndi zimene ndinakuchenjezani kale, ndikukuchenjezaninso kuti anthu amene amachita zimenezi sadzalowa mu Ufumu wa Mulungu.+

22 Koma makhalidwe amene anthu amakhala nawo mothandizidwa ndi mzimu woyera* ndi chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, kukoma mtima, ubwino,+ chikhulupiriro, 23 kufatsa ndi kudziletsa.+ Palibe lamulo loletsa makhalidwe amenewa. 24 Ndiponso anthu amene ndi ophunzira a Khristu Yesu, anakhomerera pamtengo thupi lawo pamodzi ndi zimene limakhumba komanso zimene limalakalaka.+

25 Ngati tikutsogoleredwa ndi mzimu pa moyo wathu, tiyeni tipitirize kuchita zinthu mogwirizana ndi mzimuwo.+ 26 Tisakhale odzikuza,+ tisamayambitse mpikisano pakati pathu+ komanso tisamachitirane kaduka.

6 Abale, ngati munthu wapatuka nʼkuyamba kulowera njira yolakwika mosazindikira, inu amene ndi oyenerera mwauzimu, yesani kuthandiza munthu woteroyo ndi mzimu wofatsa.+ Koma pamene mukuchita zimenezi musamale,+ kuopera kuti inunso mungayesedwe.+ 2 Pitirizani kunyamulirana zinthu zolemera.+ Mukamachita zimenezi mudzakhala mukukwaniritsa chilamulo cha Khristu.+ 3 Chifukwa ngati wina akudziona kuti ndi wofunika pamene si wotero,+ akudzinamiza yekha. 4 Koma aliyense payekha ayese zochita zake kuti aone kuti ndi zotani.+ Akatero adzakhala ndi chifukwa chosangalalira ndi zimene akuchitazo, osati modziyerekezera ndi munthu wina.+ 5 Chifukwa aliyense ayenera kunyamula katundu wake.*+

6 Komanso, aliyense amene akuphunzitsidwa mawuwo agawane zinthu zonse zabwino ndi amene akumuphunzitsayo.+

7 Musadzinamize, Mulungu sapusitsika. Chilichonse chimene munthu wafesa, adzakololanso chomwecho.+ 8 Chifukwa amene akufesa nʼcholinga chopindulitsa thupi lake, adzakolola chiwonongeko kuchokera mʼthupi lakelo, koma amene akutsatira mzimu wa Mulungu adzakolola moyo wosatha kuchokera ku mzimuwo.+ 9 Choncho tisasiye kuchita zabwino, chifukwa pa nthawi yake tidzakolola tikapanda kutopa.*+ 10 Ndiye ngati tingathe, tiyeni tichitire onse zabwino, koma makamaka abale ndi alongo athu mʼchikhulupiriro.

11 Taonani zilembo zikuluzikulu zimene ndakulemberani ndi dzanja langali.

12 Onse amene akufuna kuti azioneka ngati abwino pamaso pa anthu ndi amene akukuumirizani kuti mudulidwe. Iwo akuchita zimenezi kuti asazunzidwe chifukwa cha mtengo wozunzikirapo* wa Khristu. 13 Chifukwa ngakhale amene akudulidwawo sikuti amasunga Chilamulo,+ koma akufuna kuti inuyo mudulidwe nʼcholinga choti azidzitama chifukwa cha zimene zachitika pathupi lanu. 14 Ineyo sindikufuna kudzitama pa chifukwa china chilichonse, kupatulapo chifukwa cha mtengo wozunzikirapo* wa Ambuye wathu Yesu Khristu.+ Kwa ine, dziko linaweruzidwa kuti liphedwe* kudzera mwa iye, koma malinga nʼkuona kwa dzikoli, ineyo ndinaweruzidwa kuti ndiphedwe kudzera mwa iye. 15 Chifukwa kudulidwa kapena kusadulidwa nʼkosafunika,+ koma chofunika ndi kukhala wolengedwa mwatsopano.+ 16 Koma onse amene amatsatira lamulo limeneli la mmene tiyenera kukhalira, amene ndi Isiraeli wa Mulungu,+ akhale ndi mtendere ndipo Mulungu awasonyeze chifundo.

17 Kuyambira tsopano, pasapezeke munthu wondivutitsa, chifukwa thupi langali lili ndi zidindo zosonyeza kuti ndine kapolo wa Yesu.+

18 Abale, kukoma mtima kwakukulu kwa Ambuye wathu Yesu Khristu kukhale nanu chifukwa cha mzimu umene mumasonyeza. Ame.

Kapena kuti, “ku nthawi yoipayi.” Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Kapena kuti, “mwapatutsidwa mwamsanga.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “ndi anthu a thupi la nyama ndi magazi.”

Amene ankadziwikanso kuti Petulo.

Mʼchilankhulo choyambirira, “chikhulupiriro.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “kwa ola limodzi.”

Amene ankadziwikanso kuti Petulo.

Amene ankadziwikanso kuti Petulo.

Kapena kuti, “ndinamutsutsa.”

Kapena kuti, “zachinyengo.”

Kapena kuti, “zachinyengozi.”

Amene ankadziwikanso kuti Petulo.

Kapena kuti, “Sindikukankhira kumbali.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mundiuze.”

Onani Zakumapeto A5.

Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu yake.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu zako.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu yako.”

Kapena kuti, “mbewu.”

Kapena kuti, “wotitsogolera.”

Kapena kuti, “wotitsogolerayo.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “chifukwa tinali akapolo a zinthu zachibwanabwana zamʼdzikoli.”

Awa ndi mawu a Chiheberi kapena Chiaramu amene amatanthauza kuti, “Inu Bambo anga!”

Kapena kuti, “kundilavulira.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Izi zikanachititsa kuti akhale osayenerera kuchita zimene chilamulo chomwe ankalimbikitsacho chimanena.

Kapena kuti, “chakwaniritsidwa.”

MʼChigiriki por·nei′a. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

MʼChigiriki a·sel′gei·a. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Kapena kuti, “kuchita zamatsenga.”

Mawu a Chigiriki amene amasuliridwa kuti “kumwa mwauchidakwa” amatanthauza kumwa mowa kwambiri ndiponso mosadziletsa nʼcholinga chofuna kuledzera.

Kapena kuti, “maphwando aphokoso.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Koma chipatso cha mzimu.”

Kapena kuti, “katundu yemwe ndi udindo wake.”

Kapena kuti, “kusiya.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Kapena kuti, “lipachikidwe pamtengo.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena