Ekisodo
25 Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti:+ 2 “Uza ana a Isiraeli kuti apereke zopereka kwa ine. Anthu inu mulandire zopereka zanga kwa munthu aliyense amene mtima wake wamulimbikitsa.+ 3 Zopereka zimene muyenera kulandira kwa iwo ndi izi: golide,+ siliva,+ mkuwa,+ 4 ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wofiirira, ulusi wofiira kwambiri, nsalu zabwino kwambiri, ndi ubweya wa mbuzi.+ 5 Mulandirenso kwa iwo zikopa za nkhosa zonyika mu utoto wofiira, zikopa za akatumbu,* matabwa a mthethe,+ 6 mafuta a nyale,+ mafuta a basamu+ opangira mafuta odzozera,+ ndi zofukiza zonunkhira.+ 7 Komanso mulandire miyala ya onekisi ndi miyala yozika pa efodi*+ ndi pachovala pachifuwa.+ 8 Ndipo mundipangire malo opatulika, popeza ndiyenera kukhala pakati panu.+ 9 Mukapange chihema chopatulika ndi ziwiya zake mogwirizana ndendende ndi zonse zimene ndikukusonyeza.+
10 “Mundipangire Likasa la mtengo wa mthethe,+ mikono* iwiri ndi hafu m’litali, mkono umodzi ndi hafu m’lifupi, ndi mkono umodzi ndi hafu msinkhu wake. 11 Kenako ulikute ndi golide woyenga bwino.+ Mkati ndi kunja komwe ulikute ndi golide, ndipo upange mkombero wagolide kuzungulira Likasalo.+ 12 Ulipangire mphete zinayi zagolide ndi kuziika pamwamba pa miyendo yake inayi. Mphete ziwiri zikhale mbali imodzi, ndipo mphete zina ziwiri zikhale mbali inayo.+ 13 Upangenso mitengo yonyamulira ya mtengo wa mthethe ndi kuikuta ndi golide.+ 14 Ulowetse mitengo yonyamulirayo mumphete zija za m’mbali mwa Likasa kuti azinyamulira Likasalo. 15 Mitengo yonyamulirayo izikhala mumphete za Likasalo. Isachotsedwemo.+ 16 M’Likasamo uikemo umboni umene ndidzakupatsa.+
17 “Kenako upange chivundikiro chagolide woyenga bwino, mikono iwiri ndi hafu m’litali, ndi mkono umodzi ndi hafu m’lifupi.+ 18 Upangenso akerubi awiri agolide. Akhale osula ndipo uwaike kumapeto onse awiri a chivundikirocho.+ 19 Uike kerubi mmodzi kumbali imodzi ya chivundikirocho ndi kerubi wina kumbali inayo.+ Akerubiwo uwaike kumbali zonse ziwiri za chivundikirocho. 20 Ndipo akweze mapiko awo m’mwamba ali otambasula, aphimbe chivundikirocho ndi mapiko awo, ndipo akhale moyang’anizana,+ koma nkhope zawo ziweramire pachivundikiro. 21 Chivundikirocho+ uchiike pamwamba pa Likasalo, ndipo m’Likasamo uikemo umboni umene ndidzakupatsa. 22 Ine ndidzaonekera kwa iwe pamenepo ndi kulankhula nawe kuchokera pamwamba pa chivundikiro,+ pakati pa akerubi awiriwo amene ali pamwamba pa likasa la umboni. Kuchokera pamenepo ndidzakulamula zonse zokhudza ana a Isiraeli.+
23 “Ndiyeno upange tebulo+ la mtengo wa mthethe, mikono iwiri m’litali, mkono umodzi m’lifupi ndi mkono umodzi ndi hafu msinkhu wake. 24 Ulikute ndi golide woyenga bwino, ndipo upange mkombero wagolide kuzungulira tebulo lonselo.+ 25 Ulipangirenso felemu, muyezo wake chikhatho* chimodzi m’lifupi mwake. Felemuli lizungulire tebulo lonse ndipo upange mkombero wagolide pafelemulo.+ 26 Tebulolo ulipangire mphete zinayi zagolide ndi kuziika m’makona ake anayi mmene muli miyendo yake inayi.+ 27 Mphetezo zikhale pafupi ndi felemu lija kuti muzilowa mitengo yonyamulira tebulolo.+ 28 Upangenso mitengo yonyamulira ya mtengo wa mthethe ndi kuikuta ndi golide. Mitengo imeneyi azinyamulira tebulolo.+
29 “Ndiyeno upange mbale zake, zikho, mitsuko ndi mbale zolowa zoti azithirira nsembe zachakumwa. Uzipange ndi golide woyenga bwino.+ 30 Ndipo patebulopo uziikapo mkate wachionetsero pamaso panga nthawi zonse.+
31 “Kenako upange choikapo nyale chagolide woyenga bwino. Chimenechi chikhale chosula.+ Choikapo nyalecho chikhale ndi tsinde, nthambi, masamba ofunga duwa, mfundo ndi maluwa. 32 Choikapo nyalecho chikhale ndi nthambi 6, kumbali ina kutuluke nthambi zitatu, ndipo kumbali inayo kutulukenso nthambi zitatu.+ 33 Pamalo atatu a nthambi za mbali imodzi, pakhale masamba ofunga duwa opangidwa ngati maluwa a mtengo wa amondi, ndipo masambawo atsatizane ndi mfundo ndi maluwa. Pamalo atatu a nthambi za mbali inayo, pakhalenso masamba ofunga duwa opangidwa ngati maluwa a mtengo wa amondi, ndipo masambawo atsatizane ndi mfundo ndi maluwa.+ Nthambi 6 zotuluka m’choikapo nyalecho zikhale zotero. 34 Ndipo pamalo anayi a choikapo nyalecho pakhale masamba ofunga duwa opangidwa ngati maluwa a mtengo wa amondi, ndipo masambawo atsatizane ndi mfundo ndi maluwa.+ 35 Mfundo imodzi ikhale pansi pa nthambi zake ziwiri, mfundo ina ikhalenso pansi pa nthambi zake ziwiri, ndipo mfundo inanso ikhale pansi pa nthambi zinanso ziwiri. Zikhale choncho ndi nthambi 6 zotuluka m’choikapo nyale.+ 36 Choikapo nyalecho chikhale ndi mfundo ndi nthambi. Chonsechi chisulidwe monga chiwiya chimodzi, chagolide woyenga bwino.+ 37 Ndipo uchipangire nyale 7. Nyalezo ziziyatsidwa kuti ziziunikira patsogolo pake.+ 38 Zopanira zake zozimitsira nyale ndi mbale zake zoikamo phulusa la zingwe za nyale, zikhale zagolide woyenga bwino.+ 39 Choikapo nyalecho pamodzi ndi ziwiya zake zonsezi azipange pogwiritsa ntchito golide woyenga bwino wolemera talente limodzi.* 40 Uonetsetse kuti wazipanga motsatira chitsanzo chimene wasonyezedwa m’phiri.+