KALATA YOYAMBA YOPITA KWA TIMOTEYO
1 Ndine Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu molamulidwa ndi Mulungu amene ndi Mpulumutsi wathu komanso molamulidwa ndi Khristu Yesu, yemwe ndi chiyembekezo chathu.+ 2 Ndikukulembera iwe Timoteyo,*+ mwana wanga weniweni+ mʼchikhulupiriro:
Mulungu Atate wathu ndi Khristu Yesu Ambuye wathu akupatse kukoma mtima kwakukulu, chifundo ndi mtendere.
3 Nditatsala pangʼono kupita ku Makedoniya, ndinakupempha kuti ukhalebe ku Efeso. Ndikukupemphanso kuti ukhalebe komweko nʼcholinga choti uletse anthu ena kuti asamaphunzitse zosiyana ndi zimene timaphunzitsa, 4 ndiponso kuti asamamvere nkhani zonama+ ndi zofufuzana mibadwo ya makolo.* Zimenezi nʼzosathandiza,+ koma zimangoyambitsa nkhani zopanda umboni ndipo siziphunzitsa anthu chilichonse chochokera kwa Mulungu chokhudza chikhulupiriro. 5 Cholinga cha malangizo amenewa nʼchakuti tikhale ndi chikondi+ chochokera mumtima woyera, mʼchikumbumtima chabwino ndiponso mʼchikhulupiriro+ chopanda chinyengo. 6 Anthu ena akana kutsatira zimenezi ndipo asocheretsedwa nʼkuyamba kutsatira nkhani zopanda pake.+ 7 Anthu amenewa amafuna kukhala aphunzitsi+ a chilamulo koma samvetsa zimene akunena kapena mfundo zimene akuzilimbikira.
8 Tikudziwa kuti Chilamulo nʼchabwino ngati munthu akuchigwiritsa ntchito moyenera. 9 Ndipotu lamulo siliikidwa chifukwa cha munthu wolungama. Koma limaikidwa chifukwa cha anthu osamvera malamulo,+ oukira, osaopa Mulungu, ochimwa, osakhulupirika, onyoza zinthu zopatulika, opha abambo ndi amayi awo, opha anthu, 10 achiwerewere,* amuna amene amagonana ndi amuna anzawo, oba anthu, abodza, olumbira monama ndiponso ochita china chilichonse chosagwirizana ndi mfundo zolondola zimene Mulungu amaphunzitsa.+ 11 Mfundozi nʼzogwirizana ndi uthenga wabwino waulemerero wochokera kwa Mulungu wachimwemwe, umene anauika mʼmanja mwanga.+
12 Ndikuthokoza Khristu Yesu Ambuye wathu, amene anandipatsa mphamvu nʼkundipatsanso utumiki chifukwa anaona kuti ndine wokhulupirika.+ 13 Anatero ngakhale kuti kale ndinali wonyoza Mulungu, wozunza anthu ake ndiponso wachipongwe.+ Komabe anandichitira chifundo chifukwa ndinkachita zinthu mosadziwa komanso ndinalibe chikhulupiriro. 14 Koma ndinalandira kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu Ambuye wathu. Ndinalandiranso chikhulupiriro ndi chikondi cha Khristu Yesu. 15 Mawu akuti Khristu Yesu anabwera mʼdziko kudzapulumutsa ochimwa,+ ndi mawu oona komanso oyenera kuwavomereza ndi mtima wonse. Pa ochimwa amenewa, ine ndiye wochimwa kwambiri.+ 16 Komabe, ndinachitiridwa chifundo kuti Khristu Yesu asonyeze kuleza mtima kwake konse kudzera mwa ine wochimwa kwambiri, kuti chikhale chitsanzo kwa amene adzamukhulupirire nʼcholinga choti adzapeze moyo wosatha.+
17 Kwa Mulungu yekhayo+ yemwe ndi Mfumu yamuyaya,+ amene saafa+ komanso wosaoneka,+ kukhale ulemu ndi ulemerero mpaka kalekale. Ame.
18 Mwana wanga Timoteyo, ndikukulangiza kuchita zimenezi mogwirizana ndi maulosi amene ananeneratu za iwe, kuti mogwirizana ndi maulosiwo upitirize kumenya nkhondo yabwino.+ 19 Ukhale ndi chikhulupiriro komanso chikumbumtima chabwino+ chimene anthu ena asiya kuchitsatira, moti chikhulupiriro chawo chasweka ngati ngalawa. 20 Ena mwa anthuwa ndi Hemenayo+ ndi Alekizanda, ndipo ndawapereka kwa Satana+ kuti akalangidwa, aphunzirepo kanthu nʼkusiya kunyoza Mulungu.
2 Choyamba, ndikulimbikitsa anthu onse kuti azipemphera, kupereka mapembedzero, kupemphererana ndiponso kupereka mapemphero oyamika Mulungu mʼmalo mwa anthu osiyanasiyana. 2 Komanso mʼmalo mwa mafumu ndi anthu onse audindo wapamwamba,+ kuti tipitirize kukhala mwabata ndiponso mwamtendere komanso odzipereka kwambiri kwa Mulungu ndi oganiza bwino.+ 3 Zimenezi ndi zabwino ndiponso zovomerezeka kwa Mulungu, yemwe ndi Mpulumutsi wathu,+ 4 amene amafuna kuti anthu osiyanasiyana apulumuke+ nʼkukhala odziwa choonadi molondola. 5 Chifukwa pali Mulungu mmodzi+ ndiponso mkhalapakati mmodzi+ pakati pa Mulungu ndi anthu.+ Mkhalapakatiyu ndi Khristu Yesu,+ munthu 6 amene anadzipereka kuti akhale dipo* la anthu onse lokwanira ndendende.+ Zimenezi ndi zimene zidzachitiridwe umboni pa nthawi yake. 7 Chifukwa cha umboni umenewu,+ ine ndinasankhidwa kuti ndikhale mlaliki ndi mtumwi.+ Ndikunenatu zoona, sindikunama ayi. Ndinasankhidwa kuti ndiziphunzitsa anthu a mitundu ina+ za chikhulupiriro ndi choonadi.
8 Choncho, ndikufuna kuti kulikonse amuna apitirize kupemphera. Azikweza manja mʼmwamba mokhulupirika kwa Mulungu,+ popanda kukwiya+ ndi kutsutsana.+ 9 Nawonso akazi ayenera kudzikongoletsa ndi zovala zoyenera, povala mwaulemu ndiponso mwanzeru osati kumangodzikongoletsa ndi masitayilo omangira tsitsi, golide, ngale, kapena zovala zamtengo wapatali.+ 10 Koma azidzikongoletsa mogwirizana ndi mmene akazi odzipereka kwa Mulungu amayenera kudzikongoletsera.+ Azidzikongoletsa ndi ntchito zabwino.
11 Pophunzira, mkazi azikhala chete ndipo azigonjera ndi mtima wonse.+ 12 Sindikulola kuti mkazi aziphunzitsa kapena kulamulira mwamuna, koma azikhala chete.+ 13 Chifukwa Adamu ndi amene anayamba kupangidwa kenako Hava.+ 14 Komanso Adamu sanapusitsidwe, koma mkaziyo ndi amene anapusitsidwa+ ndipo anachimwa. 15 Komabe, mkazi adzatetezeka akabereka ana+ ngati akupitiriza kukhala ndi chikhulupiriro, chikondi komanso kukhala woyera ndiponso woganiza bwino.+
3 Mawu awa ndi oona: Ngati munthu akuyesetsa kuti akhale woyangʼanira,+ akufuna ntchito yabwino. 2 Choncho woyangʼanira ayenera kukhala wopanda chifukwa chomunenezera, mwamuna wa mkazi mmodzi, wosachita zinthu mopitirira malire, woganiza bwino,+ wochita zinthu mwadongosolo, wochereza alendo+ ndiponso wodziwa kuphunzitsa.+ 3 Asakhale munthu womwa mowa mwauchidakwa,+ kapena wankhanza,* koma wololera.+ Asakhalenso wokonda kukangana+ kapena wokonda ndalama.+ 4 Akhale mwamuna woyangʼanira bwino banja lake ndiponso woti ana ake amamumvera ndi mtima wonse.+ 5 (Ngati munthu sadziwa kuyangʼanira banja lake, ndiye mpingo wa Mulungu angausamalire bwanji?) 6 Asakhale woti wangobatizidwa kumene,*+ kuopera kuti angayambe kudzitukumula chifukwa cha kunyada nʼkulandira chiweruzo chofanana ndi chimene Mdyerekezi analandira. 7 Akhalenso ndi mbiri yabwino kwa osakhulupirira*+ kuti asanyozedwe ndi anthu komanso kukodwa mumsampha wa Mdyerekezi.
8 Nawonso atumiki othandiza akhale opanda chibwana, osanena pawiri,* osamwa vinyo wambiri ndiponso osakonda kupeza phindu mwachinyengo.+ 9 Akhale ogwira chinsinsi chopatulika cha chikhulupiriro, ali ndi chikumbumtima choyera.+
10 Ndiponso amenewa ayesedwe kaye ngati ali oyenerera, ndipo akakhala opanda chifukwa chowanenezera angakhale atumiki.+
11 Nawonso akazi akhale opanda chibwana, ochita zinthu mosapitirira malire, okhulupirika pa zinthu zonse+ ndipo asakhale amiseche.+
12 Atumiki othandiza akhale amuna a mkazi mmodzi, oyangʼanira bwino ana awo ndi mabanja awo. 13 Chifukwa amuna amene amatumikira bwino amakhala ndi mbiri yabwino ndi ufulu waukulu wolankhula za chikhulupiriro chimene chili mwa Khristu Yesu.
14 Ndikukhulupirira kuti ndibwera posachedwa, koma ndikukulembera zimenezi 15 kuti ngati ndingachedwe, udziwe zimene uyenera kuchita mʼnyumba ya Mulungu,+ imene ndi mpingo wa Mulungu wamoyo. Mpingowo ndi umene umalimbikitsa ndi kuteteza choonadi. 16 Kunena zoona, chinsinsi chopatulika chokhudza kukhala odzipereka kwa Mulungu kumeneku nʼchachikulu: ‘Iye anaonekera ngati munthu,+ anaonedwa kuti ndi wolungama pamene anali mzimu,+ anaonekera kwa angelo,+ analalikidwa kwa mitundu ya anthu,+ anthu padziko lapansi anamukhulupirira+ ndiponso analandiridwa kumwamba mu ulemerero.’
4 Komabe mawu ouziridwa amanena momveka bwino kuti nthawi ina mʼtsogolo, chikhulupiriro cha anthu ena chidzatha chifukwa chomvetsera mawu ouziridwa omwe ndi osocheretsa,+ ndiponso zinthu zimene ziwanda zimaphunzitsa. 2 Zimenezi zidzachitikanso chifukwa cha chinyengo cha anthu olankhula mabodza,+ amene chikumbumtima chawo chili ngati chipsera chobwera chifukwa chopsa ndi chitsulo chamoto. 3 Anthuwa amaletsa kukwatira,+ ndipo amalamula anthu kuti azisala zakudya+ zimene Mulungu anazilenga kuti anthu amene ali ndi chikhulupiriro+ ndiponso odziwa choonadi molondola azidya+ nʼkuyamikira Mulungu. 4 Chifukwa chilichonse cholengedwa ndi Mulungu nʼchabwino,+ ndipo palibe chimene chiyenera kukanidwa+ ngati munthu wayamika Mulungu pakudya, 5 popeza chimayeretsedwa ndi mawu a Mulungu ndiponso pemphero.
6 Ukamapereka malangizowa kwa abale, udzakhala mtumiki wabwino wa Khristu Yesu. Ndipo udzakula bwino ndi mawu a chikhulupiriro ndiponso chiphunzitso chabwino chimene wachitsatira mosamala.+ 7 Koma uzipewa nkhani zonama zosalemekeza Mulungu+ ngati zimene amayi ena okalamba amakamba. Mʼmalomwake, uzidziphunzitsa nʼcholinga choti ukhalebe wodzipereka kwa Mulungu. 8 Chifukwa kuchita masewera olimbitsa thupi ndi kothandiza pangʼono, koma kukhala wodzipereka kwa Mulungu ndi kothandiza pa zinthu zonse, chifukwa kumakhudza lonjezo la moyo wathu panopa ndi moyo umene ukubwerawo.+ 9 Mawu amenewa ndi oona ndipo ndi oyenera kuwavomereza ndi mtima wonse. 10 Nʼchifukwa chake tikugwira ntchito mwakhama ndiponso mwamphamvu,+ chifukwa chiyembekezo chathu chili mwa Mulungu wamoyo, amene ndi Mpulumutsi+ wa anthu onse, koma makamaka okhulupirika.+
11 Pitiriza kuwaphunzitsa ndi kuwalamula kuti azichita zimenezi. 12 Usalole kuti munthu aliyense akuderere poona kuti ndiwe wamngʼono. Mʼmalomwake, ukhale chitsanzo kwa okhulupirika pa zimene umalankhula, makhalidwe ako, chikondi, chikhulupiriro ndi khalidwe loyera. 13 Pamene ukundiyembekezera, pitiriza kukhala wodzipereka powerenga pagulu,+ polimbikitsa* anthu ndiponso pophunzitsa. 14 Usamanyalanyaze mphatso yomwe unapatsidwa mwaulosi pamene bungwe la akulu linaika manja pa iwe.+ 15 Uziganizira mozama* zinthu zimenezi ndipo uzizichita modzipereka kuti anthu onse aone kuti ukupita patsogolo. 16 Nthawi zonse uzisamala ndi zimene umachita komanso zimene umaphunzitsa.+ Pitiriza kuchita zimenezi, chifukwa ukatero udzadzipulumutsa wekha komanso anthu okumvera.+
5 Usadzudzule mokalipa mwamuna wachikulire,+ koma uzilankhula naye mokoma mtima ngati bambo ako. Amuna achinyamata uzilankhula nawo ngati achimwene ako 2 ndipo akazi achikulire ngati amayi ako. Akazi achitsikana uzilankhula nawo ngati achemwali ako, ndipo pochita zimenezi usakhale ndi maganizo alionse olakwika.
3 Uziganizira* akazi amasiye amene alidi amasiye.*+ 4 Koma ngati mkazi wamasiye ali ndi ana kapena adzukulu, iwowo akhale oyamba kusamalira anthu a mʼbanja lawo+ posonyeza kuti ndi odzipereka kwa Mulungu. Azibwezera kwa makolo ndi agogo awo zowayenerera+ chifukwa zimenezi zimakondweretsa Mulungu.+ 5 Mkazi amene alidi wamasiye, amene akusowa womusamalira, amadalira Mulungu+ ndipo amapitiriza kupemphera ndi kupembedzera masana ndi usiku.+ 6 Koma amene amangochita zinthu motsatira zilakolako zake, ndi wakufa ngakhale kuti ali moyo. 7 Choncho upitirize kuwapatsa malangizo* amenewa kuti asakhale ndi chifukwa chowanenezera. 8 Ndithudi, ngati munthu sasamalira anthu amene ndi udindo wake kuwasamalira, makamaka a mʼbanja lake, wakana chikhulupiriro ndipo ndi woipa kuposa munthu wosakhulupirira.+
9 Mkazi wamasiye wolembedwa pamndandanda wa akazi amasiye, akhale wazaka zoposa 60. Akhalenso amene anali wokhulupirika kwa mwamuna wake,* 10 wodziwika kuti anachita ntchito zabwino,+ analera bwino ana ake,+ ankachereza alendo,+ anasambitsa mapazi a oyera,+ anathandiza anthu amene anali pa mavuto+ ndiponso ankagwira modzipereka ntchito iliyonse yabwino.
11 Koma usaike akazi amasiye achitsikana pamndandanda umenewu, chifukwa ngati atengeka ndi chilakolako chofuna mwamuna mʼmalo motumikira Khristu, amasankha kukwatiwa. 12 Zikatero, amapezeka olakwa chifukwa sanasunge lonjezo lawo.* 13 Komanso amangokhala osachita kanthu nʼkumangoyendayenda mʼmakomo mwa anzawo. Kuwonjezera pa kumangokhala osachita kanthu, amakondanso miseche, kulowerera nkhani za eni+ komanso kulankhula zinthu zimene sayenera kulankhula. 14 Choncho ndingakonde kuti akazi amasiye achitsikana azikwatiwa,+ kubereka ana+ ndiponso kusamalira banja nʼcholinga choti otsutsa asatipezere chifukwa. 15 Ndipotu ena asocheretsedwa kale moti ayamba kutsatira Satana. 16 Ngati mkazi aliyense wokhulupirira ali ndi achibale amene ndi akazi amasiye, iyeyo aziwathandiza, kuti akazi amasiyewo asachititse mpingo kupanikizika. Zikatero, mpingowo ungathe kuthandiza amene alidi akazi amasiye.*+
17 Akulu amene amatsogolera bwino+ azilemekezedwa kwambiri,+ makamaka amene amachita khama polankhula Mawu a Mulungu ndiponso kuphunzitsa.+ 18 Paja Mawu a Mulungu amati: “Usamange ngʼombe pakamwa pamene ikupuntha* mbewu.”+ Komanso amati: “Wantchito ayenera kulandira malipiro ake.”+ 19 Usavomereze mlandu woneneza mwamuna wachikulire,* kupatulapo ngati pali mboni ziwiri kapena zitatu.+ 20 Anthu amene ali ndi chizolowezi chochita tchimo,+ uziwadzudzula+ pamaso pa onse kuti ena onsewo akhale ndi mantha.* 21 Ndikukulamula mwamphamvu, pamaso pa Mulungu ndi Khristu Yesu ndiponso angelo ochita kusankhidwa, kuti uzitsatira malangizo amenewa popanda tsankho kapena kukondera.+
22 Usafulumire kuika munthu aliyense pa udindo,*+ kapena kugawana ndi anthu ena machimo awo. Pitiriza kukhala ndi khalidwe loyera.
23 Usamamwenso madzi,* koma uzimwa vinyo pangʼono, chifukwa cha vuto lako la mʼmimba ndiponso kudwaladwala kwako kuja.
24 Machimo a anthu ena amadziwika kwa anthu, ndipo amaweruzidwa nthawi yomweyo. Koma anthu ena, machimo awo amadzaonekera pakapita nthawi.+ 25 Nazonso ntchito zabwino zimadziwika kwa anthu,+ ndipo zimene sizidziwika sizingabisike mpaka kalekale.+
6 Anthu onse amene ndi akapolo aziona kuti ambuye awo ndi oyenera kuwalemekeza ndi mtima wonse,+ kuti dzina la Mulungu ndiponso zimene amatiphunzitsa zisanyozedwe.+ 2 Komanso akapolo amene ambuye awo ndi Akhristu, asamawachitire zinthu mopanda ulemu poona kuti ndi abale. Mʼmalomwake, azigwira ntchito mwakhama kwambiri, chifukwa ntchito yawo yabwinoyo ikuthandiza Akhristu anzawo omwe amawakonda.
Pitiriza kuphunzitsa zinthu zimenezi ndiponso kulimbikitsa anthu kuti azichita zimenezi. 3 Ngati munthu akuphunzitsa zinthu zabodza, ndipo sakuvomereza malangizo abwino+ ochokera kwa Ambuye wathu Yesu Khristu, ndiponso zinthu zimene timaphunzira zogwirizana ndi kudzipereka kwathu kwa Mulungu,+ 4 munthu ameneyo ndi wodzitukumula ndiponso wonyada ndipo samvetsa kalikonse.+ Mʼmalomwake, amakonda kukangana ndiponso kutsutsana pa mawu.+ Zimenezi zimayambitsa nsanje, mikangano, kunenerana mawu achipongwe* ndiponso kuganizirana zoipa. 5 Zimachititsanso kuti anthu opotoka maganizo+ ndiponso osadziwa choonadi, azikangana pa zinthu zazingʼono poganiza kuti kukhala wodzipereka kwa Mulungu ndi njira yopezera phindu.+ 6 Nʼzoona kuti kukhala wodzipereka kwa Mulungu+ komanso kukhala wokhutira ndi zimene tili nazo, ndi njira yopezera phindu lalikulu. 7 Pajatu sitinabwere ndi kanthu mʼdziko ndipo sitingachokemo ndi kanthu.+ 8 Choncho, ngati tili ndi chakudya, zovala ndi pogona, tizikhala okhutira ndi zinthu zimenezi.+
9 Koma anthu ofunitsitsa kulemera amakumana ndi mayesero ndiponso amakodwa mumsampha.+ Iwo amalakalaka zinthu zowapweteketsa komanso amachita zinthu mopanda nzeru. Zimenezi zimawawononga ndiponso kuwabweretsera mavuto.+ 10 Chifukwa kukonda ndalama kumayambitsa* zopweteka za mtundu uliwonse, ndipo chifukwa chotengeka ndi chikondi chimenechi, ena asiya chikhulupiriro ndipo adzibweretsera zopweteka zambiri pathupi lawo.+
11 Koma munthu wa Mulungu iwe, thawa zinthu zimenezi. Mʼmalomwake yesetsa kukhala wachilungamo, wodzipereka kwa Mulungu, wachikhulupiriro, wachikondi, wopirira ndiponso wofatsa.+ 12 Menya nkhondo yabwino ya chikhulupiriro. Gwira mwamphamvu moyo wosatha umene anakuitanira. Paja unalengeza momveka bwino zokhudza moyo umenewu pamaso pa mboni zambiri.
13 Pamaso pa Mulungu, amene amathandiza kuti zinthu zonse zikhalebe zamoyo ndiponso pamaso pa Khristu Yesu, amene anapereka umboni wabwino kwambiri pamaso pa Pontiyo Pilato,+ ndikukulamula 14 kuti uzisunga malamulo. Uziwasunga uli woyera ndiponso wopanda chifukwa chokunenezera mpaka pamene Ambuye wathu Yesu Khristu adzaonekere.+ 15 Iye ndi wachimwemwe ndi Wamphamvu komanso ndi Mfumu ya mafumu ndi Mbuye wa ambuye,+ ndipo adzaonekera pa nthawi yake. 16 Iyeyo ali ndi moyo woti sungafe+ ndipo amakhala pamalo owala kwambiri moti palibe munthu angafikepo.+ Palibenso munthu amene anamuonapo kapena amene angamuone.+ Iye apatsidwe ulemu ndipo mphamvu zake zikhalebe mpaka kalekale. Ame.
17 Ulangize* anthu achuma mʼdzikoli* kuti asakhale odzikweza, ndiponso kuti asamadalire chuma chosadalirika,+ koma azidalira Mulungu, amene amatipatsa mowolowa manja zinthu zonse zomwe timasangalala nazo.+ 18 Uwauze kuti azichita zabwino, akhale olemera pa ntchito zabwino, owolowa manja komanso okonzeka kugawira ena+ 19 kuti asunge bwino chuma chochokera kwa Mulungu chomwe ndi maziko abwino a tsogolo+ lawo nʼcholinga choti agwire mwamphamvu moyo weniweniwo.+
20 Timoteyo, usunge bwino zimene unalandira kwa Mulungu.+ Uzipewa nkhani zopanda pake zimene zimaipitsa zinthu zoyera. Uzipewanso kutsutsana pa zinthu zimene ena monama amati ndi “kudziwa zinthu.”+ 21 Chifukwa chodzionetsera ndi kudziwa zinthu kumeneku, ena asiya chikhulupiriro.
Kukoma mtima kwakukulu kukhale nanu.
Kutanthauza “Amene Amalemekeza Mulungu.”
Kapena kuti, “kukumbana mibadwo ya makolo.”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Kapena kuti, “wandewu; wachiwawa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “wotembenuka kumene.”
Amenewa ndi anthu amene sali mumpingo wa Chikhristu.
Kapena kuti, “osalankhula mwachinyengo.”
Kapena kuti, “podandaulira.”
Kapena kuti, “Uzisinkhasinkha.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Uzilemekeza.”
Kapena kuti, “akazi amasiye amene akusowadi zinthu”; kutanthauza kuti alibe owathandiza.
Kapena kuti, “malamulo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mkazi wa mwamuna mmodzi.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “chikhulupiriro choyamba.”
Kapena kuti, “akazi amasiye amene akusowadi zinthu”; kutanthauza kuti alibe owathandiza.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Kapena kuti, “mkulu.”
Kapena kuti, “likhale chenjezo kwa ena onsewo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “kuika manja ako pa munthu.”
Kapena kuti, “Usiye kumwa madzi okha.”
Kapena kuti, “kunenezana.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ndi muzu wa.”
Kapena kuti, “Ulamule.”
Kapena kuti, “a mʼnthawi ino.” Onani Matanthauzo a Mawu Ena.