Yesaya
16 Anthu inu, tumizani nkhosa yamphongo kwa wolamulira wa dziko.+ Muitumize kuchokera ku Sela kudutsa kuchipululu mpaka kukafika kuphiri la mwana wamkazi wa Ziyoni.+
2 Pamalo owolokera chigwa cha Arinoni,+ ana aakazi a Mowabu adzakhala ngati mbalame yomwe ikuthawa, itathamangitsidwa pachisa chake.+
3 “Anthu inu, perekani malangizo. Chitani zimene zagamulidwa.+
“Chititsani kuti masana, mthunzi wanu uphimbe malo aakulu ndiponso uchititse mdima ngati wa usiku.+ Bisani anthu obalalika.+ Musaulule aliyense amene akuthawa.+ 4 Anthu anga obalalika akhale ngati alendo mwa iwe Mowabu.+ Iwo abisale mwa iwe pothawa wolanda,+ pakuti wopondereza anthu wafika pamapeto ake. Kulanda kwatha. Opondaponda anzawo atha padziko lapansi.+
5 “Mpando wachifumu ndithu udzakhazikika ndi kukoma mtima kosatha.+ Mfumu idzakhala pampandowo n’kumalamulira mokhulupirika muhema wa Davide.+ Izidzaweruza n’kumafunafuna chilungamo, ndipo izidzachita mwachangu zinthu zoyenera.”+
6 Ife tamva za kunyada kwa Mowabu, kuti ndi wonyada kwambiri.+ Tamva za kudzikweza kwake, kunyada kwake, ndi mkwiyo wake.+ Zolankhula zake zodzitukumula sizidzachitika.+ 7 Chotero Mowabu adzalira mofuula chifukwa cha tsoka lake. Aliyense wokhala m’Mowabu ndithu adzalira mofuula.+ Omenyedwawo adzalirira mphesa zouma zoumba pamodzi za ku Kiri-hareseti,+ 8 chifukwa minda ya m’mapiri ya ku Hesiboni+ yafota. Eni ake a mitundu ya anthu athyola nthambi za mitengo ya mpesa ya ku Sibima+ zodzaza ndi mphesa zakupsa. Nthambizo zinafika mpaka ku Yazeri.+ Zinafika mpaka kuchipululu. Mphukira zake zinasiyidwa kuti zizingodzikulira pazokha. Zinafika mpaka kunyanja.
9 N’chifukwa chake ndidzalirire mtengo wa mpesa wa ku Sibima ngati mmene ndinachitira polirira Yazeri.+ Ndidzakunyowetsa kwambiri ndi misozi yanga iwe Hesiboni+ ndi Eleyale,+ chifukwa chakuti kufuula kwakugwera m’chilimwe ndi pa nthawi ya zokolola zako.+ 10 Kukondwera ndi kusangalala zachotsedwa m’munda wako wa zipatso, ndipo m’minda ya mpesa mulibe mfuu yachisangalalo. Mulibe aliyense amene akufuula.+ Mopondera mphesa mulibe amene akuponda vinyo.+ Ndachititsa kuti kufuula kulekeke.+
11 N’chifukwa chake mkati mwanga mukunjenjemera ngati zingwe za zeze chifukwa cha Mowabu,+ ndipo m’mimba mwanga mukubwadamuka chifukwa cha Kiri-hareseti.+
12 Kenako zinaoneka kuti Mowabu anatopa pamalo okwezeka,+ ndipo anapita kumalo opatulika kukapemphera+ koma sizinathandize.+
13 Awa ndi mawu okhudza Mowabu amene Yehova ananena kalekale. 14 Koma tsopano Yehova wanena kuti: “Pomatha ndendende zaka zitatu,*+ ulemerero+ wa Mowabu udzatha. Iye adzachititsidwa manyazi ndipo adzakumana ndi chipwirikiti chamtundu uliwonse. Otsala mwa iye adzakhala ochepa kwambiri ndiponso opanda mphamvu.”+