KALATA YOPITA KWA AKOLOSE
1 Ine Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu mwa kufuna kwa Mulungu, ndili limodzi ndi Timoteyo+ mʼbale wathu. 2 Ndikulembera oyera ndi abale okhulupirika amene ali ogwirizana ndi Khristu ku Kolose kuti:
Mulungu Atate wathu akupatseni kukoma mtima kwakukulu ndi mtendere.
3 Nthawi zonse tikamakupemphererani, timathokoza Mulungu, Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu. 4 Timachita zimenezi chifukwa tinamva za chikhulupiriro chanu mwa Khristu Yesu komanso za chikondi chimene mukusonyeza oyera onse 5 chifukwa cha chiyembekezo chodzalandira zinthu zimene akusungirani kumwamba.+ Munamva za chiyembekezo chimenechi mʼmbuyomu pamene munamva uthenga wa choonadi, womwe ndi uthenga wabwino 6 umene unafika kwa inu. Uthenga wabwino ukubala zipatso ndiponso kufalikira padziko lonse.+ Zimenezi ndi zimenenso zakhala zikuchitika kwa inu kuyambira tsiku limene munamva ndi kudziwa molondola za kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu komwe ndi kwenikweni. 7 Zimenezi ndi zimene munaphunzira kwa Epafura,+ kapolo mnzathu wokondedwa, amene ndi mtumiki wokhulupirika wa Khristu mʼmalo mwa ife. 8 Iye ndi amenenso anatidziwitsa za chikondi chanu chimene munachisonyeza mothandizidwa ndi mzimu wa Mulungu.*
9 Nʼchifukwa chake ifenso, kuyambira tsiku limene tinamva zimenezo, sitinasiye kukupemphererani.+ Takhala tikupempha kuti mudziwe molondola+ chifuniro cha Mulungu ndiponso kuti mukhale ndi nzeru zonse komanso muzimvetsetsa zinthu zauzimu.+ 10 Tachita zimenezi nʼcholinga choti mukhale ndi khalidwe logwirizana* ndi zimene Yehova* amafuna, kuti muzimusangalatsa pa chilichonse, pamene mukupitiriza kubala zipatso pantchito iliyonse yabwino ndi kuwonjezera kumudziwa Mulungu molondola.+ 11 Tikupemphanso kuti mulandire mphamvu zazikulu mogwirizana ndi mphamvu zake zochititsa mantha,+ nʼcholinga choti muthe kupirira zinthu zonse moleza mtima ndiponso mwachimwemwe, 12 komanso muzithokoza Atate, amene anapangitsa kuti mukhale oyenerera kulandira nawo cholowa cha oyera+ amene ali mʼkuwala.
13 Iye anatipulumutsa ku ulamuliro wa mdima,+ nʼkutisamutsira mu ufumu wa Mwana wake wokondedwa. 14 Kudzera mwa Mwana wakeyo, tinamasulidwa ndi dipo* ndipo machimo athu amakhululukidwa.+ 15 Iye ndi chifaniziro cha Mulungu wosaonekayo,+ woyamba kubadwa wa chilengedwe chonse.+ 16 Kudzera mwa iye, Mulungu analenga zinthu zina zonse kumwamba ndi padziko lapansi. Analenga zinthu zooneka ndi zinthu zosaoneka,+ kaya ndi mipando yachifumu, ambuye, maboma komanso maulamuliro. Inde, analenga zinthu zina zonse kudzera mwa iye+ ndiponso chifukwa cha iye. 17 Ndiponso iye analipo kale zinthu zina zonse zisanakhaleko+ ndipo zinthu zina zonse zinakhalapo kudzera mwa iye. 18 Iye ndi mutu wa thupi, lomwe ndi mpingo.+ Iye ndi chiyambi, woyamba kubadwa kuchokera kwa akufa,+ kuti adzakhale woyamba pa zinthu zonse. 19 Zili choncho chifukwa chakuti Mulungu zinamusangalatsa kuti makhalidwe ake onse akhale mwa Khristu.+ 20 Komanso kuti kudzera mwa mwana wakeyo agwirizanitsenso zinthu zina zonse+ ndi iyeyo, kaya zinthuzo ndi zapadziko lapansi kapena zakumwamba. Anachita zimenezi pokhazikitsa mtendere kudzera mʼmagazi+ amene Khristu anakhetsa pamtengo wozunzikirapo.*
21 Ndithudi, inu amene kale munali otalikirana ndi Mulungu ndiponso adani ake chifukwa maganizo anu anali pa ntchito zoipa, 22 tsopano wagwirizana nanunso kudzera mu imfa ya mwana wake amene anapereka thupi lake lanyama nʼcholinga choti akuperekeni pamaso pa Mulunguyo, muli opatulika ndi opanda chilema ndiponso opanda chifukwa chokunenezerani.+ 23 Koma mukuyenera kupitiriza kukhala mogwirizana ndi chikhulupiriro chanu,+ muli okhazikika pamaziko,+ muli olimba+ komanso muli osasunthika pa chiyembekezo cha uthenga wabwino umene munamva, umenenso unalalikidwa padziko lonse.*+ Ineyo Paulo ndinakhala mtumiki wa uthenga wabwino umenewu.+
24 Tsopano ndikusangalala ndi mavuto amene ndikukumana nawo chifukwa cha inu.+ Ndipo inenso ndikuona kuti sindinazunzikebe mokwanira monga chiwalo cha thupi la Khristu,+ limene ndi mpingo.+ 25 Ndinakhala mtumiki wa mpingo umenewu mogwirizana ndi udindo+ umene Mulungu anandipatsa woti ndilalikire mawu a Mulungu mokwanira, kuti inuyo mupindule. 26 Mawuwo akuphatikizapo chinsinsi chopatulika+ chimene dziko silinachidziwe+ ndiponso chinali chobisika kwa mibadwo yakale. Koma tsopano chaululidwa kwa oyera ake.+ 27 Mulungu zinamusangalatsa kuululira oyera pakati pa anthu a mitundu ina chinsinsi chopatulikachi,+ chomwe chili ndi ulemerero wochuluka komanso chuma chauzimu. Chinsinsi chimenechi ndi Khristu amene ndi wogwirizana ndi inuyo, kutanthauza kuti muli ndi chiyembekezo chodzalandira ulemerero limodzi ndi Khristuyo.+ 28 Tikulengeza, kuchenjeza ndi kuphunzitsa munthu aliyense za iyeyu mu nzeru zonse, kuti tipereke munthu aliyense kwa Mulungu ali wolimba mwauzimu mogwirizana ndi Khristu.+ 29 Kuti ndikwanitse kuchita zimenezi, ndikugwira ntchito mwakhama ndipo ndikuyesetsa kwambiri podalira mphamvu zake zimene zikugwira ntchito mwamphamvu mwa ine.+
2 Ndikufuna kuti mudziwe mavuto aakulu amene ndikukumana nawo chifukwa cha inuyo ndi anthu a ku Laodikaya+ komanso chifukwa cha anthu onse amene sanandionepo maso ndi maso.* 2 Ndikuchita zimenezi kuti mitima yawo ilimbikitsidwe+ ndiponso kuti onse akhale ogwirizana mʼchikondi+ komanso kuti alandire chuma chonse chimene chimabwera chifukwa chomvetsa bwino zinthu, popanda kukayikira chilichonse, nʼcholinga choti adziwe molondola chinsinsi chopatulika cha Mulungu, chomwe ndi Khristu.+ 3 Chuma chonse chokhudzana ndi nzeru ndiponso kudziwa zinthu chinabisidwa mosamala mwa iye.+ 4 Ndikunena zimenezi kuti munthu aliyense asakupusitseni ndi mfundo zokopa. 5 Ngakhale kuti sindili kumeneko, ndikuganizirabe za inu. Ndasangalala kumva kuti mumachita zinthu mwadongosolo+ komanso kuti muli ndi chikhulupiriro cholimba mwa Khristu.+
6 Tsopano popeza mumakhulupirira Khristu Yesu Ambuye wathu, pitirizani kuyenda mogwirizana naye. 7 Mogwirizana ndi zimene munaphunzira, chikhulupiriro chanu mwa Khristu chikhale ndi mizu yolimba, chipitirize kukula+ ndipo chikhale cholimba+ komanso nthawi zonse muzithokoza Mulungu.+
8 Samalani kuti wina asakugwireni ukapolo,* pogwiritsa ntchito nzeru za anthu ndi chinyengo chopanda pake,+ mogwirizana ndi miyambo ya anthu komanso mfundo zimene anthu amʼdzikoli amayendera, osati mogwirizana ndi Khristu, 9 chifukwa iye ali ndi makhalidwe onse a Mulungu.+ 10 Simukusowa kalikonse chifukwa cha iye, amene ndi mutu wa boma lililonse ndi ulamuliro uliwonse.+ 11 Popeza muli naye pa ubwenzi munadulidwa ndipo mdulidwe wake sunali wochitidwa ndi manja a anthu koma unachitika pamene munavula thupi lauchimo,+ chifukwa mdulidwe wa atumiki a Khristu umakhala wotero.+ 12 Zili choncho chifukwa munaikidwa naye limodzi mʼmanda pobatizidwa ubatizo wofanana ndi wake.+ Ndipo popeza muli naye pa ubwenzi komanso mumakhulupirira zinthu zimene Mulungu, amene anamuukitsa kwa akufa+ anapanga ndi mphamvu zake, munaukitsidwa naye limodzi.+
13 Kuwonjezera pamenepo, ngakhale kuti munali akufa chifukwa cha machimo anu komanso chifukwa choti munali osadulidwa, Mulungu anakupatsani moyo kuti mukhale ogwirizana ndi Khristu.+ Mokoma mtima anatikhululukira machimo athu onse+ 14 ndipo anafafaniza Chilamulo+ chimene chinali ndi malamulo ambirimbiri+ omwe ankatitsutsa.+ Iye anachichotsa pochikhomerera pamtengo wozunzikirapo.*+ 15 Pogwiritsa ntchito mtengo wozunzikirapowo, iye anavula maboma ndi olamulira nʼkuwasiya osavala ndipo anawaonetsa poyera kuti anthu onse aone kuti wawagonjetsa+ nʼkumayenda nawo ngati akaidi.
16 Choncho musalole kuti munthu aliyense akuweruzeni chifukwa cha chakudya ndi chakumwa+ kapena chikondwerero chinachake kapenanso kusunga tsiku limene mwezi watsopano waoneka+ kapena kusunga sabata.+ 17 Zinthu zimenezi ndi mthunzi wa zimene zinali kubwera,+ koma zenizeni zake zinakwaniritsidwa ndi Khristu.+ 18 Musalole kuti munthu aliyense amene amasangalala ndi kudzichepetsa kwachinyengo komanso kulambira angelo* akulepheretseni kudzalandira mphoto.+ “Munthu woteroyo amaumirira” zinthu zimene waona ndipo maganizo ake ochimwa amamuchititsa kuti azidzitukumula popanda chifukwa chomveka. 19 Sakutsatira amene ndi mutu,+ amene kudzera mwa iye, thupi lonse limapeza zonse zimene limafunikira ndipo ziwalo zake ndi zolumikizana bwino ndi mfundo zake komanso minyewa ndipo limakulabe mothandizidwa ndi Mulungu.+
20 Ngati munafa limodzi ndi Khristu ndipo simukutsatiranso mfundo zimene anthu amʼdzikoli amayendera,+ nʼchifukwa chiyani mukupitiriza kukhala ngati mudakali mbali ya dzikoli, pogonjeranso malamulo akuti:+ 21 “Usatenge ichi, kapena usalawe ichi, kapena usakhudze ichi”? 22 Malamulo amenewa akunena za zinthu zimene zimatha munthu akamazigwiritsa ntchito ndipo ndi malamulo komanso zinthu zimene anthu amaphunzitsa.+ 23 Ngakhale kuti zinthu zimenezo zimaoneka ngati zanzeru, amene amazichitawo amasankha okha njira yolambirira. Iwo amazunza thupi lawo+ kuti anthu aziona ngati ndi odzichepetsa. Koma zimenezo nʼzosathandiza kwa munthu amene akulimbana ndi zimene thupi limalakalaka.
3 Komabe, ngati munaukitsidwa limodzi ndi Khristu,+ pitirizani kufunafuna zinthu zakumwamba, kumene Khristu wakhala kudzanja lamanja la Mulungu.+ 2 Pitirizani kuganizira zinthu zakumwamba,+ osati zinthu zapadziko lapansi.+ 3 Chifukwa munafa ndipo moyo wanu wabisidwa limodzi ndi Khristu amene ndi wogwirizana ndi Mulungu. 4 Khristu, amene ndi moyo wathu,+ akadzaonetsa mphamvu zake,* inunso mudzaonetsa naye limodzi mphamvu zanu mu ulemerero.+
5 Choncho chititsani ziwalo za thupi lanu+ padziko lapansi kukhala zakufa ku chiwerewere,* zinthu zodetsa, chilakolako chosalamulirika cha kugonana,+ kulakalaka zinthu zoipa komanso dyera limene ndi kulambira mafano. 6 Mulungu adzasonyeza mkwiyo wake kwa anthu amene akuchita zimenezi. 7 Inunso munkachita zomwezo, pamene munkakhala moyo wofanana ndi anthu amenewo.+ 8 Koma tsopano muyenera kutaya zonsezo kutali ndi inu. Mutaye mkwiyo, kupsa mtima, kuipa+ komanso mawu achipongwe+ ndipo pakamwa panu pasatuluke nkhani zotukwana.+ 9 Musamanamizane.+ Vulani umunthu* wakale+ pamodzi ndi ntchito zake, 10 ndipo muvale umunthu watsopano+ umene Mulungu amapereka. Umunthu watsopano umenewu ndi wopangidwa mogwirizana ndi chifaniziro cha Mulungu.+ Choncho pamene mukudziwa Mulungu molondola, pitirizani kuchititsa umunthu wanu kukhala watsopano. 11 Mukatero, sipadzakhala Mgiriki kapena Myuda, kudulidwa kapena kusadulidwa, mlendo, Msukuti,* kapolo kapena mfulu, chifukwa Khristu amachita zinthu zonse ndipo ife ndife ogwirizana naye.+
12 Choncho monga anthu osankhidwa ndi Mulungu,+ oyera ndi okondedwa, valani chifundo chachikulu,+ kukoma mtima, kudzichepetsa,+ kufatsa+ komanso kuleza mtima.+ 13 Pitirizani kulolerana ndi kukhululukirana ndi mtima wonse,+ ngakhale pamene wina ali ndi chifukwa chodandaulira za mnzake.+ Mofanana ndi Yehova* amene anakukhululukirani ndi mtima wonse, inunso muzichita chimodzimodzi.+ 14 Koma kuwonjezera pa zonsezi, valani chikondi,+ chifukwa chimagwirizanitsa anthu mwamphamvu kwambiri kuposa chinthu china chilichonse.+
15 Komanso lolani kuti mtendere wa Khristu ulamulire mʼmitima yanu,+ popeza munaitanidwa ku mtendere umenewu monga ziwalo za thupi limodzi. Ndipo sonyezani kuti ndinu oyamikira. 16 Mawu a Khristu akhazikike mwa inu ndipo akupatseni nzeru zonse. Pitirizani kuphunzitsana ndi kulimbikitsana* ndi masalimo,+ nyimbo zotamanda Mulungu komanso nyimbo zauzimu zoyamikira. Pitirizani kuimbira Yehova* mʼmitima yanu.+ 17 Chilichonse chimene mukuchita mʼmawu kapena mu ntchito, muzichita zonse mʼdzina la Ambuye Yesu, ndipo muziyamika Mulungu Atate kudzera mwa iye.+
18 Inu akazi, muzigonjera amuna anu,+ chifukwa zimenezi ndi zoyenera kwa anthu otsatira Ambuye. 19 Inu amuna, pitirizani kukonda akazi anu+ ndipo musamawapsere mtima kwambiri.*+ 20 Ana inu, muzimvera makolo anu pa zinthu zonse,+ chifukwa zimenezi zimasangalatsa Ambuye. 21 Inu abambo, musamakwiyitse* ana anu,+ kuti asakhale okhumudwa. 22 Inu akapolo, muzimvera anthu amene ndi ambuye anu+ pa zinthu zonse, osati pokhapokha pamene akukuonani pongofuna kusangalatsa anthu,* koma moona mtima ndiponso moopa Yehova.* 23 Chilichonse chimene mukuchita, muzichichita ndi moyo wanu wonse ngati kuti mukuchitira Yehova,*+ osati anthu, 24 chifukwa mukudziwa kuti mphoto imene mudzalandire ndi cholowa chochokera kwa Yehova.*+ Tumikirani Ambuye wanu Khristu monga akapolo. 25 Ndithudi, amene akuchita zolakwa adzalandira chilango chifukwa cha zolakwa zimene akuchitazo,+ chifukwa Mulungu sakondera.+
4 Inu anthu amene ndinu ambuye, muzichitira akapolo anu zinthu zachilungamo ndi zoyenera, chifukwa mukudziwa kuti inunso muli ndi Ambuye kumwamba.+
2 Muzilimbikira kupemphera.+ Mukhale maso pa nkhani ya kupemphera ndipo muziyamikira.+ 3 Komanso muzitipempherera ifeyo+ kuti Mulungu atitsegulire khomo kuti tithe kulalikira mawu ndi kulankhula za chinsinsi chopatulika chokhudza Khristu, chimene chinachititsa kuti ndimangidwe nʼkukhala mʼndende muno,+ 4 kuti ndidzalalikire za chinsinsicho momveka bwino ngati mmene ndiyenera kuchitira.
5 Pitirizani kuchita zinthu mwanzeru pamene mukukhala ndi anthu akunja, ndipo muzigwiritsa ntchito bwino nthawi yanu.*+ 6 Nthawi zonse mawu anu azisonyeza kuti ndinu okoma mtima ndipo azikhala okoma ngati kuti mwawathira mchere,+ kuti mudziwe mmene mungayankhire munthu aliyense.+
7 Tukiko+ amene ndi mʼbale wanga wokondedwa, mtumiki wokhulupirika komanso kapolo mnzanga mwa Ambuye, adzakuuzani zonse zokhudza ine. 8 Ndikumutumiza kwa inu kuti mudziwe mmene tilili komanso kuti alimbikitse mitima yanu. 9 Abwera limodzi ndi Onesimo,+ mʼbale wanga wokhulupirika ndi wokondedwa, amene anachokera pakati panu. Iwo adzakuuzani zonse zimene zikuchitika kuno.
10 Arisitako+ mkaidi mnzanga akuti moni nonse. Komanso Maliko+ msuweni wa Baranaba, (amene ndinakulangizani kuti mumulandire+ nthawi iliyonse akadzafika kwa inu), 11 ndi Yesu, amene amadziwikanso kuti Yusito, akuti moni. Iwowa ali mʼgulu la anthu odulidwa. Amenewa okha ndi antchito anzanga pa zinthu zokhudzana ndi Ufumu wa Mulungu ndipo amandilimbikitsa kwambiri. 12 Epafura,+ amene anachokera pakati panu, kapolo wa Khristu Yesu, akuti moni. Iye amakupemphererani mwakhama nthawi zonse kuti mupitirize kukhala olimba mwauzimu komanso kuti musamakayikire ngakhale pangʼono zinthu zonse zimene Mulungu adzachite. 13 Ndikumuchitiradi umboni kuti amadzipereka kwambiri chifukwa cha inu komanso chifukwa cha abale a ku Laodikaya ndi ku Herapoli.
14 Luka,+ dokotala wokondedwa, akuti moni nonse. Dema+ nayenso akupereka moni. 15 Mundiperekere moni kwa abale a ku Laodikaya komanso kwa Numfa ndi mpingo umene umasonkhana panyumba pake.+ 16 Kalatayi mukaiwerenga kwanuko, konzani zoti ikawerengedwenso+ kumpingo wa Alaodikaya, ndiponso kuti inuyo muwerenge yochokera ku Laodikaya. 17 Komanso Arikipo+ mumuuze kuti: “Uonetsetse kuti utumiki umene unaulandira mwa Ambuye ukuukwaniritsa.”
18 Tsopano landirani moni wanga wolemba ndekha ndi dzanja langa,+ ineyo Paulo. Pitirizani kukumbukira maunyolo amene andimanga nawo kundende kuno.+ Kukoma mtima kwakukulu kukhale nanu.
Mʼchilankhulo choyambirira, “mumzimu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “muziyenda mogwirizana.”
Onani Zakumapeto A5.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼchilengedwe chonse cha pansi pa thambo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “amene sanaonepo nkhope yanga.”
Kapena kuti, “asakugwireni ngati nyama.”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Kapena kuti, “kulambira ngati mmene angelo amachitira.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “akadzaonetsedwa.”
MʼChigiriki por·nei′a. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mʼchilankhulo choyambirira, “munthu.”
Mawu akuti “Msukuti” akutanthauza munthu wachimidzimidzi.
Onani Zakumapeto A5.
Kapena kuti, “kulangizana.”
Onani Zakumapeto A5.
Kapena kuti, “ndipo musamawachitire nkhanza.”
Kapena kuti, “musamapsetse mtima.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “osati mwachiphamaso ngati munthu wongofuna kusangalatsa anthu.”
Onani Zakumapeto A5.
Onani Zakumapeto A5.
Onani Zakumapeto A5.
Mʼchilankhulo choyambirira, “ndipo muzigula nthawi yoikidwiratu.”