Nehemiya
7 Ndiyeno mpanda utangotha kumangidwanso,+ ndinaika zitseko zake.+ Kenako ndinaika alonda a m’zipata,+ oimba+ ndi Alevi.+ 2 Zitatero ndinaika Haneni+ m’bale wanga ndi Hananiya kalonga wa m’Nyumba ya Chitetezo Champhamvu,+ kuti aziyang’anira Yerusalemu. Hananiya anali munthu wodalirika+ ndipo anali woopa kwambiri+ Mulungu woona kuposa anthu ena ambiri. 3 Choncho ndinawauza kuti: “Zipata+ za Yerusalemu siziyenera kutsegulidwa kufikira dzuwa litatentha. Alonda a m’zipatazo atseke zitseko ndi kuzikhoma ndi akapichi ndipo aime pafupi.+ Muikenso alonda a anthu okhala mu Yerusalemu, ena muwaike pamalo awo olondera ndipo ena muwaike kutsogolo kwa nyumba zawo.”+ 4 Tsopano mzindawo unali wotakasuka ndi waukulu. Mkati mwake munali anthu ochepa+ ndipo sanamangemo nyumba.
5 Koma Mulungu wanga anaika nzeru mumtima mwanga+ kuti ndisonkhanitse anthu olemekezeka, atsogoleri ndi anthu onse kuti alembetse mayina awo motsatira mzere wawo wobadwira.+ Ndiyeno ndinapeza buku la mndandanda wa mayina a mzere wobadwira+ wa anthu amene anabwera moyambirira kuchokera ku ukapolo. Ndinapeza kuti m’bukumo analembamo izi:
6 Awa ndi anthu a m’chigawo+ amene anatuluka mu ukapolo+ wa anthu omwe Nebukadinezara+ mfumu ya ku Babulo anawatengera ku ukapolo ku Babulo.+ Anthuwa anabwerera ku Yerusalemu ndi ku Yuda, aliyense kumzinda wakwawo.+ 7 Amenewa anabwera pamodzi ndi Zerubabele,+ Yesuwa,+ Nehemiya, Azariya,* Raamiya,* Nahamani, Moredekai,+ Bilisani, Misiperete,* Bigivai, Nehumu,* ndi Bana.
Chiwerengero cha amuna a Isiraeli ndi ichi: 8 Ana a Parosi,+ 2,172. 9 Ana a Sefatiya,+ 372. 10 Ana a Ara,+ 652. 11 Ana a Pahati-mowabu,+ ochokera mwa ana a Yesuwa ndi Yowabu,+ 2,818. 12 Ana a Elamu,+ 1,254. 13 Ana a Zatu,+ 845. 14 Ana a Zakai,+ 760. 15 Ana a Binui,+ 648. 16 Ana a Bebai,+ 628. 17 Ana a Azigadi,+ 2,322. 18 Ana a Adonikamu,+ 667. 19 Ana a Bigivai,+ 2,067. 20 Ana a Adini,+ 655. 21 Ana a Ateri,+ a m’nyumba ya Hezekiya, 98. 22 Ana a Hasumu,+ 328. 23 Ana a Bezai,+ 324. 24 Ana a Harifi,+ 112. 25 Ana a Gibeoni,+ 95. 26 Amuna a ku Betelehemu+ ndi ku Netofa,+ 188. 27 Amuna a ku Anatoti,+ 128. 28 Amuna a ku Beti-azimaveti,+ 42. 29 Amuna a ku Kiriyati-yearimu,+ Kefira,+ ndi ku Beeroti,+ 743. 30 Amuna a ku Rama+ ndi ku Geba,+ 621. 31 Amuna a ku Mikemasi,+ 122. 32 Amuna a ku Beteli+ ndi ku Ai,+ 123. 33 Amuna a ku Nebo wina,+ 52. 34 Ana a Elamu wina,+ 1,254. 35 Ana a Harimu,+ 320. 36 Ana a Yeriko,+ 345. 37 Ana a Lodi,+ Hadidi+ ndi Ono,+ 721. 38 Ana a Senaya,+ 3,930.
39 Ansembe: Ana a Yedaya,+ a m’nyumba ya Yesuwa, 973. 40 Ana a Imeri,+ 1,052. 41 Ana a Pasuri,+ 1,247. 42 Ana a Harimu,+ 1,017.
43 Alevi: Ana a Yesuwa, a m’nyumba ya Kadimiyeli+ ochokera pakati pa ana a Hodeva,+ 74. 44 Oimba,+ ana a Asafu,+ 148. 45 Alonda a pachipata,+ ana a Salumu,+ ana a Ateri, ana a Talimoni,+ ana a Akubu,+ ana a Hatita, ana a Sobai,+ 138.
46 Anetini:+ Ana a Ziha, ana a Hasufa, ana a Tabaoti,+ 47 ana a Kerosi, ana a Siya,* ana a Padoni,+ 48 ana a Lebana, ana a Hagaba,+ ana a Salimai, 49 ana a Hanani,+ ana a Gideli, ana a Gahara, 50 ana a Reyaya,+ ana a Rezini,+ ana a Nekoda, 51 ana a Gazamu, ana a Uziza, ana a Paseya, 52 ana a Besai,+ ana a Meyuni, ana a Nefusesimu,*+ 53 ana a Bakibuki, ana a Hakufa, ana a Harihuri,+ 54 ana a Baziliti,* ana a Mehida, ana a Harisa,+ 55 ana a Barikosi, ana a Sisera, ana a Tema,+ 56 ana a Neziya, ana a Hatifa.+
57 Ana a atumiki a Solomo:+ Ana a Sotai, ana a Sofereti, ana a Perida,*+ 58 ana a Yaala, ana a Darikoni, ana a Gideli,+ 59 ana a Sefatiya, ana a Hatili, ana a Pokereti-hazebaimu, ana a Amoni.*+ 60 Anetini onse+ pamodzi ndi ana a atumiki a Solomo analipo 392.
61 Ndiyeno amene anachokera ku Tele-mela, Tele-harisa, Kerubi, Adoni ndi Imeri,+ ndipo sanathe kufotokoza mzere wa makolo awo ndi kumene anachokera, kuti kaya anali ochokera mu Isiraeli kapena ayi, ndi awa: 62 ana a Delaya, ana a Tobia, ana a Nekoda,+ 642. 63 Ansembe+ anali awa: ana a Habaya, ana a Hakozi+ ana a Barizilai+ amene anatenga mkazi pakati pa ana aakazi a Barizilai+ Mgiliyadi ndipo anayamba kutchedwa ndi dzina lawo. 64 Amenewa ndiwo anayang’ana mayina awo m’kaundula kuti atsimikizire anthu onse za mzere wawo wobadwira koma sanawapeze.+ Zitatero anawaletsa kuti asatumikire monga ansembe chifukwa anali oipitsidwa.+ 65 Pa chifukwa chimenechi, Tirisata*+ anawauza kuti sayenera kudya+ zinthu zopatulika koposa kufikira patakhala wansembe wokhala ndi Urimu+ ndi Tumimu.+
66 Mpingo wonsewo monga gulu limodzi unali ndi anthu 42,360,+ 67 kupatulapo akapolo awo aamuna+ ndi akapolo awo aakazi amene analipo 7,337.+ Iwo analinso ndi oimba aamuna+ ndi aakazi+ 245. 68 Anali ndi mahatchi 736 ndi nyulu* 245.+ 69 Ngamila+ zinalipo 435. Abulu analipo 6,720.+
70 Ndiye panali atsogoleri+ ena a nyumba za makolo+ amene anapereka mphatso zothandizira pa ntchito.+ Tirisata+ anapereka ndalama za dalakima* zagolide 1,000, mbale zikuluzikulu 50, ndi mikanjo ya ansembe 530 kumalo osungira chuma.+ 71 Ndiyeno panalinso atsogoleri ena a nyumba za makolo amene anapereka mphatso zothandizira pa ntchitoyo kumalo osungira chuma. Iwo anapereka ndalama za dalakima zagolide 20,000, ndi ndalama za mina* zasiliva 2,200.+ 72 Zimene anthu ena onse anapereka zinakwana ndalama za dalakima zagolide 20,000, ndalama za mina zasiliva 2,000 ndi mikanjo ya ansembe 67.
73 Ndiyeno ansembe,+ Alevi, alonda a pazipata, oimba,+ anthu ena onse pamodzi ndi Anetini+ ndi Isiraeli yense anapita kukakhala m’mizinda yawo.+ Pofika mwezi wa 7+ ana a Isiraeli anali atakhala m’mizinda yawo.+