Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • nwt Daniel 1:1-12:13
  • Danieli

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Danieli
  • Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Danieli

DANIELI

1 Mʼchaka chachitatu cha ufumu wa Mfumu Yehoyakimu+ ya Yuda, Mfumu Nebukadinezara ya ku Babulo inabwera ku Yerusalemu ndipo inazungulira mzindawo.+ 2 Kenako Yehova anapereka Mfumu Yehoyakimu ya Yuda mʼmanja mwake,+ limodzi ndi zina mwa ziwiya za mʼnyumba ya* Mulungu woona. Nebukadinezara anatenga ziwiyazo nʼkupita nazo kudziko la Sinara,*+ kunyumba* ya mulungu wake ndipo anakaziika mʼnyumba yosungiramo chuma ya mulungu wake.+

3 Ndiyeno mfumu inalamula Asipenazi, mkulu wa nduna zapanyumba ya mfumu kuti abweretse ena mwa Aisiraeli,* kuphatikizapo a mʼbanja lachifumu komanso anthu olemekezeka.+ 4 Inalamula kuti abweretse achinyamata* amene analibe chilema chilichonse, ooneka bwino, anzeru, odziwa zinthu, ozindikira+ komanso amene akanatha kutumikira mʼnyumba ya mfumu. Iye ankayenera kuwaphunzitsa chilankhulo komanso zinthu zina zimene Akasidi analemba. 5 Kuwonjezera pamenepo, mfumu inalamula kuti tsiku lililonse aziwapatsa zakudya zabwino za mfumu ndi vinyo wofanana ndi amene mfumu inkamwa. Ankayenera kuwaphunzitsa* kwa zaka zitatu ndipo pambuyo pa zaka zimenezi, ankayenera kuyamba kutumikira mfumu.

6 Pagulu la anyamatawo panali anyamata ena a fuko la Yuda.* Mayina awo anali Danieli,*+ Hananiya,* Misayeli* ndi Azariya.*+ 7 Mkulu wa nduna zapanyumba ya mfumu anapatsa anyamatawa mayina* ena. Danieli anamupatsa dzina lakuti Belitesazara,+ Hananiya anamupatsa dzina lakuti Shadireki,* Misayeli anamupatsa dzina lakuti Misheki* ndipo Azariya anamupatsa dzina lakuti Abedinego.+

8 Koma Danieli anatsimikiza mumtima mwake kuti sadzidetsa ndi zakudya zabwino za mfumu kapena ndi vinyo amene ankamwa. Choncho iye anapempha mkulu wa nduna zapanyumba ya mfumu kuti amulole kuti asadzidetse ndi zinthu zimenezi. 9 Choncho Mulungu woona anachititsa kuti mkulu wa nduna zapanyumba ya mfumu akomere mtima Danieli komanso kumusonyeza chifundo.+ 10 Mkulu wa nduna zapanyumba ya mfumuyo anauza Danieli kuti: “Ine ndikuopa mbuye wanga mfumu, amene walamula kuti muzipatsidwa chakudya ndi zakumwa zimenezi. Ndiye mukuona kuti zitha bwanji akakuonani kuti ndinu owonda kuposa anyamata* ena a msinkhu wanu? Mupangitsa kuti ndikhale* ndi mlandu pamaso pa mfumu.” 11 Koma Danieli anauza munthu amene ankawayangʼanira uja, yemwe mkulu wa nduna zapanyumba ya mfumu anamuika kuti aziyangʼanira Danieli, Hananiya, Misayeli ndi Azariya. Iye anati: 12 “Chonde, mutiyese atumiki anufe kwa masiku 10 ndipo mulole kuti tizipatsidwa zakudya zamasamba ndi madzi akumwa. 13 Kenako mudzayerekeze mmene ifeyo tikuonekera ndi mmene anyamata* amene akudya zakudya zabwino za mfumu akuonekera, ndipo mudzachitire atumiki anufe mogwirizana ndi zimene mudzaone.”

14 Choncho munthu amene ankawayangʼanira uja anavomera kuchita zimene anamupemphazo ndipo anawayesa kwa masiku 10. 15 Masiku 10 amenewo atatha, iwo ankaoneka bwino kwambiri ndipo anali athanzi* kuposa anyamata* onse amene ankadya zakudya zabwino za mfumu. 16 Choncho, amene ankawayangʼanira uja anapitirizabe kuwapatsa zakudya zamasamba mʼmalo mwa zakudya zabwino za mfumu ndi vinyo wake. 17 Mulungu woona anachititsa kuti anyamata* 4 amenewa akhale odziwa zinthu komanso ozindikira zinthu zonse zolembedwa ndipo anawapatsa nzeru. Danieli anamupatsa nzeru zoti azitha kumvetsa bwino masomphenya ndi maloto amtundu uliwonse.+

18 Masiku amene mfumu inanena kuti adzabweretse anyamata aja pamaso pake atakwana,+ mkulu wa nduna zapanyumba ya mfumu uja anabweretsa anyamatawo pamaso pa Nebukadinezara. 19 Mfumuyo italankhula nawo, inaona kuti pagulu lonselo panalibe aliyense amene ankafanana ndi Danieli, Hananiya, Misayeli ndi Azariya.+ Choncho anyamata amenewa anapitiriza kutumikira mfumu. 20 Pa nkhani iliyonse yofunika nzeru komanso kuzindikira, imene mfumu inkawafunsa, inaona kuti iwo anali anzeru kuwirikiza maulendo 10 kuposa ansembe onse ochita zamatsenga ndi anthu onse olankhula ndi mizimu+ amene anali mu ufumu wake wonse. 21 Choncho Danieli anapitiriza kukhala kumeneko mpaka chaka choyamba cha ulamuliro wa Mfumu Koresi.+

2 Mʼchaka chachiwiri cha ufumu wake, Nebukadinezara analota maloto angapo, moti anavutika maganizo+ ndipo tulo tinamuthera. 2 Choncho mfumuyo inalamula kuti aitane ansembe onse ochita zamatsenga, anthu olankhula ndi mizimu, Akasidi* ndi anthu ena ochita zamatsenga kuti adzauze mfumu maloto akewo. Anthu amenewa anafika nʼkuima pamaso pa mfumu.+ 3 Ndiyeno mfumuyo inawauza kuti: “Ine ndalota maloto ndipo ndikuvutika maganizo kwambiri chifukwa ndikufuna kudziwa zimene ndalotazo.” 4 Akasidi anayankha mfumu mʼchinenero cha Chiaramu*+ kuti: “Inu mfumu mukhale ndi moyo mpaka kalekale. Tiuzeni ife atumiki anu zimene mwalota ndipo tikumasulirani malotowo.”

5 Mfumuyo inayankha Akasidiwo kuti: “Ndikukuuzani komaliza kuti: Ngati simundiuza zimene ndalota nʼkundimasulira, ndikudulani nthulinthuli ndipo nyumba zanu ndidzazisandutsa zimbudzi za anthu onse.* 6 Koma mukandiuza malotowo nʼkuwamasulira, ine ndikupatsani mphatso, mphoto ndi ulemerero waukulu.+ Choncho ndiuzeni malotowo ndipo muwamasulire.”

7 Iwo anayankha kachiwiri kuti: “Inu mfumu, tiuzeni ife atumiki anu zimene mwalota ndipo ife tikumasulirani malotowo.”

8 Ndiyeno mfumuyo inanena kuti: “Ine ndikudziwa kuti mukuzengereza dala kuti mukhale ndi nthawi yambiri yoganiza chifukwa mukudziwa kale zimene ndalamula. 9 Mukapanda kundiuza malotowo, chilango chimene nonsenu mulandire chikhala chofanana. Koma mwagwirizana kuti mundiuze zabodza komanso zachinyengo mpaka zinthu zitasintha. Ndiye ndiuzeni zimene ndalota ndipo mukatero, ndidziwa kuti mungathe kumasulira malotowo.”

10 Akasidiwo anayankha mfumuyo kuti: “Palibe munthu padziko lapansi amene angathe kuchita zimene inu mfumu mukufuna. Palibe mfumu yaikulu kapena bwanamkubwa amene anauzapo wansembe wochita zamatsenga, munthu wolankhula ndi mizimu kapena Mkasidi kuti achite zimenezi. 11 Zimene inu mfumu mukufuna kuti tichite ndi zovuta, ndipo palibe munthu amene angakuuzeni maloto anu kupatulapo milungu, imene sikhala pakati pa anthu.”

12 Mfumu itamva zimenezi inakwiya kwambiri ndipo inalamula kuti amuna onse anzeru a mʼBabulo aphedwe.+ 13 Lamulo limenelo litaperekedwa ndipo amuna anzeru atatsala pangʼono kuphedwa, anthu anayambanso kufunafuna Danieli ndi anzake kuti awaphe.

14 Pa nthawi imeneyo Danieli analankhula mwanzeru komanso mosamala kwambiri ndi Arioki mkulu wa asilikali olondera mfumu, amene anali atanyamuka kale kuti akaphe amuna anzeru a mʼBabulo. 15 Iye anafunsa Arioki mkulu wa asilikali olondera mfumu uja kuti: “Nʼchifukwa chiyani mfumu yapereka lamulo lokhwima chonchi?” Ndiyeno Arioki anafotokozera Danieli zonse zimene zinachitika.+ 16 Choncho Danieli anapita kwa mfumu kukapempha kuti imupatse nthawi kuti adzamasulire maloto ake.

17 Kenako Danieli anabwerera kunyumba kwake ndipo anauza anzake aja, Hananiya, Misayeli ndi Azariya za nkhani imeneyi. 18 Iye anawapempha kuti apemphere kwa Mulungu wakumwamba kuti awachitire chifundo nʼkuwaululira chinsinsi chimenechi, kuti Danieli ndi anzakewo asaphedwe limodzi ndi amuna ena onse anzeru a mʼBabulo.

19 Ndiyeno usiku, chinsinsicho chinaululidwa kwa Danieli mʼmasomphenya.+ Choncho Danieli anatamanda Mulungu wakumwamba. 20 Iye anati:

“Dzina la Mulungu litamandike mpaka kalekale,*

Chifukwa nzeru ndi mphamvu ndi zake.+

21 Iye amasintha nthawi ndi nyengo,+

Amachotsa mafumu komanso kuika mafumu,+

Amapereka nzeru kwa anthu anzeru ndiponso amachititsa kuti anthu ozindikira adziwe zinthu.+

22 Amaulula zinthu zozama ndi zinthu zobisika,+

Amadziwa zinthu zimene zili mumdima,+

Ndipo iye wazunguliridwa ndi kuwala.+

23 Ndikukutamandani komanso kukuyamikani, inu Mulungu wa makolo anga,

Chifukwa mwandipatsa nzeru ndi mphamvu.

Ndipo tsopano mwandiuza zimene tinakupemphani,

Mwatidziwitsa zinthu zimene mfumu ikuda nazo nkhawa.”+

24 Kenako Danieli anapita kwa Arioki amene anatumidwa ndi mfumu kuti aphe amuna anzeru a ku Babulo+ ndipo anamuuza kuti: “Musaphe mwamuna aliyense wanzeru mʼBabulo. Ndipititseni kwa mfumu ndipo ine ndikamasulira maloto ake.”

25 Mofulumira, Arioki anapititsa Danieli kwa mfumu nʼkuiuza kuti: “Ndapeza munthu pakati pa anthu amene anatengedwa ukapolo ku Yuda+ yemwe angamasulire maloto anu mfumu.” 26 Mfumuyo inafunsa Danieli, amene dzina lake linali Belitesazara+ kuti: “Kodi ungathedi kundiuza maloto amene ndinalota komanso kuwamasulira?”+ 27 Danieli anayankha mfumuyo kuti: “Palibe amuna anzeru, anthu olankhula ndi mizimu, ansembe ochita zamatsenga kapena anthu okhulupirira nyenyezi amene angakwanitse kukuuzani inu mfumu chinsinsi chimene mukufuna kudziwa.+ 28 Koma kumwamba kuli Mulungu amene ndi Woulula zinsinsi,+ ndipo wakudziwitsani inu Mfumu Nebukadinezara zimene zidzachitike mʼmasiku otsiriza. Maloto anu komanso masomphenya amene munaona muli pabedi lanu ndi awa:

29 Inu mfumu, mutagona pabedi lanu munayamba kuganiza za zinthu zimene zidzachitike mʼtsogolo ndipo Mulungu amene ndi Woulula zinsinsi wakudziwitsani zimene zidzachitike. 30 Sikuti chinsinsi chimenechi chaululidwa kwa ine chifukwa chakuti ndine wanzeru kuposa munthu wina aliyense, koma chaululidwa nʼcholinga chakuti ndikumasulireni malotowo inu mfumu ndiponso kuti mudziwe maganizo amumtima mwanu.+

31 Inuyo mfumu munalota mukuona chifaniziro chachikulu kwambiri. Chifanizirocho chinali chitaima patsogolo panu ndipo chinali chachikulu komanso chowala kwambiri ndipo chimaoneka mochititsa mantha. 32 Mutu wa chifanizirocho unali wagolide wabwino kwambiri,+ pachifuwa pake ndi manja ake zinali zasiliva,+ mimba yake ndi ntchafu zake zinali zakopa,*+ 33 miyendo yake inali yachitsulo+ ndipo mapazi ake anali achitsulo chosakanikirana ndi dongo.+ 34 Munapitiriza kuyangʼana mpaka mwala unadulidwa kuphiri koma osati ndi manja a munthu. Mwalawo unamenya chifanizirocho kumapazi ake achitsulo chosakanikirana ndi dongo nʼkuwaphwanya.+ 35 Pa nthawi imeneyo chitsulo, dongo, kopa, siliva ndi golide, zonse zinaphwanyikaphwanyika ndipo zinakhala ngati mankhusu* apamalo opunthirapo mbewu mʼchilimwe. Mphepo inaziuluza moti sizinaonekenso. Koma mwala umene unamenya chifanizirocho unakhala phiri lalikulu ndipo linadzaza dziko lonse lapansi.

36 Maloto anu ndi amenewa mfumu ndipo tsopano tikuuzani kumasulira kwake. 37 Inuyo mfumu yomwe ndi mfumu ya mafumu, amene Mulungu wakumwamba wakupatsani ufumu,+ mphamvu ndi ulemerero, 38 inuyo amene Mulungu wakupatsani mphamvu zolamulira anthu kulikonse kumene akukhala komanso nyama zakutchire ndi mbalame zamumlengalenga, amene Mulungu wakuikani kuti muzilamulira zonsezi,+ inuyo ndi mutu wagolide.+

39 Koma pambuyo panu padzabwera ufumu+ wina wotsikirapo kwa inu. Kenako padzabweranso ufumu wina wachitatu, wakopa, umene udzalamulire dziko lonse lapansi.+

40 Ufumu wa nambala 4 udzakhala wolimba ngati chitsulo.+ Mofanana ndi chitsulo chimene chimaphwanya nʼkupera china chilichonse, ufumuwo udzaphwanya nʼkuwonongeratu maufumu ena onsewa.+

41 Mogwirizana ndi zimene munaona kuti mapazi ndi zala zakumiyendo zinali zadongo la woumba mbiya losakanikirana ndi chitsulo, ufumuwo udzakhala wogawanika. Koma udzakhala wolimba pa zinthu zina ngati chitsulo, ngati mmene munaonera kuti chitsulocho chinali chosakanikirana ndi dongo lofewa. 42 Popeza zala zakumiyendo zinali zachitsulo chosakanikirana ndi dongo, pa zinthu zina ufumuwo udzakhala wolimba koma pa zinthu zina udzakhala wosalimba. 43 Mogwirizana ndi zimene munaona kuti chitsulo chinasakanikirana ndi dongo lofewa, mbali zake zina zidzasakanikirana ndi anthu* koma sadzagwirizana mofanana ndi mmene zimakhalira kuti chitsulo sichingasakanikirane bwinobwino ndi dongo.

44 Mʼmasiku a mafumu amenewo, Mulungu wakumwamba adzakhazikitsa ufumu+ umene sudzawonongedwa.+ Ufumu umenewu sudzaperekedwa kwa anthu a mtundu wina uliwonse.+ Koma udzaphwanya nʼkuthetsa maufumu ena onsewa+ ndipo ndi ufumu wokhawu umene udzakhalepo mpaka kalekale.+ 45 Zidzachitika mogwirizana ndi zimene munaona kuti mwala unadulidwa kuphiri koma osati ndi manja a munthu ndipo unaphwanya chitsulo, kopa, dongo, siliva ndi golide.+ Inu mfumu, Mulungu Wamkulu wakudziwitsani zimene zidzachitike mʼtsogolo.+ Maloto amenewa adzakwaniritsidwa ndithu ndipo kumasulira kwake nʼkodalirika.”

46 Ndiyeno Mfumu Nebukadinezara anagwada nʼkuwerama mpaka nkhope yake pansi pamaso pa Danieli nʼkumupatsa ulemu. Iye analamula kuti Danieli apatsidwe mphatso komanso kuti amufukizire zofukiza zonunkhira. 47 Mfumuyo inauza Danieli kuti: “Ndithudi Mulungu wanu ndi Mulungu wa milungu, Ambuye wa mafumu komanso Woulula zinsinsi, chifukwa iwe wakwanitsa kuulula chinsinsi chimenechi.”+ 48 Kenako mfumu inamukweza pa udindo Danieli ndipo inamupatsa mphatso zambiri zabwino. Inamuikanso kuti akhale wolamulira wa chigawo chonse cha Babulo+ ndiponso mkulu wa akuluakulu a boma amene ankayangʼanira amuna onse anzeru a mʼBabulo. 49 Ndipo Danieli anapempha mfumu kuti iike Shadireki,* Misheki* ndi Abedinego+ kuti akhale oyangʼanira ntchito za boma mʼchigawo cha Babulo, ndipo mfumuyo inawaikadi. Koma Danieli ankagwira ntchito kunyumba ya mfumu.

3 Mfumu Nebukadinezara inapanga fano lagolide limene linali lalitali mikono 60* ndipo mulifupi mwake linali mikono 6.* Fanoli analiimika mʼchigwa cha Dura, mʼchigawo cha Babulo. 2 Kenako Mfumu Nebukadinezara inatumiza uthenga kwa masatarapi,* akuluakulu a boma, abwanamkubwa, alangizi, asungichuma, oweruza, akuluakulu a zamalamulo ndi oyangʼanira onse a zigawo kuti asonkhane kumwambo wotsegulira fano limene Mfumu Nebukadinezara inaimika.

3 Choncho masatarapi, akuluakulu a boma, abwanamkubwa, alangizi, asungichuma, oweruza, akuluakulu a zamalamulo ndi oyangʼanira onse a zigawo, anasonkhana kumwambo wotsegulira fano limene Mfumu Nebukadinezara inaimika. Iwo anaimirira patsogolo pa fano limene Nebukadinezara anaimika. 4 Wolengeza mauthenga anafuula kuti: “Mfumu ikukulamulani, inu anthu a mitundu yosiyanasiyana komanso olankhula zinenero zosiyanasiyana, 5 kuti mukangomva kulira kwa lipenga, chitoliro, zeze wamngʼono, zeze wamakona atatu, choimbira chazingwe, chitoliro chathumba ndi zipangizo zina zonse zoimbira, mugwade nʼkuwerama mpaka nkhope zanu pansi ndipo mulambire fano lagolide limene Mfumu Nebukadinezara yaimika. 6 Aliyense amene sagwada nʼkuwerama mpaka nkhope yake pansi nʼkulambira fanolo, nthawi yomweyo aponyedwa mungʼanjo yoyaka moto.”+ 7 Choncho anthu onse atangomva kulira kwa lipenga, chitoliro, zeze wamngʼono, zeze wamakona atatu, choimbira chazingwe ndi zipangizo zina zonse zoimbira, anthu onse a mitundu yosiyanasiyana komanso olankhula zinenero zosiyanasiyana, anagwada nʼkulambira fano lagolide limene Mfumu Nebukadinezara inaimika.

8 Pa nthawi imeneyo, Akasidi ena anapita kwa mfumu kukaneneza* Ayuda. 9 Iwo anauza Mfumu Nebukadinezara kuti: “Inu mfumu, mukhale ndi moyo mpaka kalekale. 10 Inuyo mfumu munalamula kuti munthu aliyense akamva kulira kwa lipenga, chitoliro, zeze wamngʼono, zeze wamakona atatu, choimbira chazingwe, chitoliro chathumba ndi zipangizo zina zonse zoimbira, agwade nʼkulambira fano lagolide. 11 Munalamulanso kuti aliyense amene sagwada nʼkuwerama mpaka nkhope yake pansi nʼkulambira fanolo aponyedwe mungʼanjo yoyaka moto.+ 12 Koma pali Ayuda ena amene munawaika kuti aziyangʼanira ntchito za boma mʼchigawo cha Babulo. Amuna amenewa ndi Shadireki,* Misheki* ndi Abedinego.+ Iwo sakukumverani inu mfumu ndipo sakutumikira milungu yanu moti akukana kulambira fano lagolide limene mwaimika.”

13 Ndiyeno Nebukadinezara anapsa mtima kwambiri ndipo analamula kuti abweretse Shadireki, Misheki ndi Abedinego. Choncho anabweretsadi amuna amenewa pamaso pa mfumu. 14 Nebukadinezara anawafunsa kuti: “Kodi ndi zoonadi kuti inu Shadireki, Misheki ndi Abedinego simukutumikira milungu yanga+ komanso kuti mukukana kulambira fano lagolide limene ndaimika? 15 Ndiye ngati ndinu okonzeka kugwada nʼkulambira fano lagolide, mukamva kulira kwa lipenga, chitoliro, zeze wamngʼono, zeze wamakona atatu, choimbira chazingwe, chitoliro chathumba ndi zipangizo zina zonse zoimbira, zili bwino. Koma mukakana kulambira, nthawi yomweyo muponyedwa mungʼanjo yoyaka moto. Ndipo ndi mulungu uti amene angakupulumutseni mʼmanja mwanga?”+

16 Ndiye Shadireki, Misheki ndi Abedinego anayankha mfumuyo kuti: “Inu Mfumu Nebukadinezara, palibenso china chimene ife tinganene kwa inu pa nkhani imeneyi. 17 Ngati mungatiponyere mungʼanjo yoyaka moto, Mulungu wathu amene tikumutumikira akhoza kutipulumutsa. Iye akhozanso kutipulumutsa mʼmanja mwanu mfumu.+ 18 Koma ngakhale atapanda kutipulumutsa, dziwani mfumu kuti ife sititumikira milungu yanu kapena kulambira fano lagolide limene mwaimika.”+

19 Pamenepo Nebukadinezara anapsa mtima kwambiri ndi Shadireki, Misheki ndi Abedinego ndipo nkhope yake inasintha.* Iye analamula kuti ngʼanjoyo aisonkhezere kuwirikiza ka 7 kuposa mmene ankachitira nthawi zonse. 20 Iye analamula asilikali ake ena amphamvu kuti amange Shadireki, Misheki ndi Abedinego nʼkuwaponya mungʼanjo yoyaka motoyo.

21 Choncho amuna amenewa anamangidwa atavala nsalu zawo zakunja, zovala zawo, zipewa zawo ndi zovala zawo zina zonse ndipo anawaponya mungʼanjo yoyaka moto ija. 22 Koma chifukwa chakuti mfumu inalamula zimenezi itapsa mtima kwambiri komanso ngʼanjo ya motoyo inali yotentha kwambiri, asilikali amene anatenga Shadireki, Misheki ndi Abedinego aja ndi amene anaphedwa ndi malawi a moto. 23 Koma amuna atatuwa, Shadireki, Misheki ndi Abedinego, anagwera mungʼanjo ya motoyo ali omangidwa.

24 Ndiyeno Mfumu Nebukadinezara inachita mantha kwambiri ndipo inanyamuka mwachangu nʼkufunsa nduna zake zapamwamba kuti: “Kodi sitinaponye amuna atatu pamoto titawamanga?” Ndunazo zinayankha mfumuyo kuti: “Inde, mfumu.” 25 Ndiyeno mfumu inati: “Taonani! Inetu ndikuona amuna 4 akuyendayenda pakati pa moto ali osamangidwa komanso sakupsa, ndipo munthu wa 4 akuoneka ngati mwana wa milungu.”

26 Nebukadinezara anayandikira khomo la ngʼanjo yoyaka motoyo nʼkunena kuti: “Shadireki, Misheki ndi Abedinego, inu atumiki a Mulungu Wamʼmwambamwamba,+ tulukani ndipo mubwere kuno!” Atatero, Shadireki, Misheki ndi Abedinego anatuluka pakati pa motowo. 27 Masatarapi, akuluakulu a boma, abwanamkubwa ndi nduna zapamwamba za mfumu amene anasonkhana kumeneko,+ anaona kuti amuna amenewa+ motowo sunawawotche* ngakhale pangʼono. Tsitsi la kumutu kwawo ndi limodzi lomwe silinawauke. Zovala zawo sizinasinthe ndipo sankamveka ngakhale fungo la moto.

28 Kenako Nebukadinezara ananena kuti: “Atamandike Mulungu wa Shadireki, Misheki ndi Abedinego+ amene anatumiza mngelo wake nʼkudzapulumutsa atumiki ake. Atumiki akewo anamudalira ndipo sanamvere lamulo la mfumu, moti anali okonzeka kufa* mʼmalo motumikira kapena kulambira mulungu wina aliyense kupatulapo Mulungu wawo.+ 29 Choncho ine ndikuika lamulo lakuti, anthu a mtundu uliwonse kapena olankhula zinenero zosiyanasiyana amene anganene chilichonse chotsutsana ndi Mulungu wa Shadireki, Misheki ndi Abedinego ayenera kudulidwa nthulinthuli ndipo nyumba zawo zisandutsidwe zimbudzi za anthu onse,* chifukwa palibe mulungu wina amene amatha kupulumutsa anthu ake mofanana ndi ameneyu.”+

30 Kenako mfumu inakweza paudindo* Shadireki, Misheki ndi Abedinego mʼchigawo cha Babulo.+

4 “Uwu ndi uthenga wochokera kwa ine Mfumu Nebukadinezara wopita kwa anthu a mitundu yosiyanasiyana komanso olankhula zinenero zosiyanasiyana amene akukhala padziko lonse lapansi: Mukhale ndi mtendere wochuluka. 2 Ndine wosangalala kukuuzani zizindikiro ndi zodabwitsa zimene Mulungu Wamʼmwambamwamba wandichitira. 3 Zizindikiro zake nʼzazikulu ndipo zochita zake nʼzamphamvu. Ufumu wake udzakhalapo mpaka kalekale ndipo ulamuliro wake udzakhalapo ku mibadwomibadwo.+

4 Ine Nebukadinezara ndinkakhala mwabata mʼnyumba mwanga ndipo zinthu zinkandiyendera bwino mʼnyumba yanga yachifumu. 5 Ndiyeno ndinalota maloto amene anandichititsa mantha. Nditagona pabedi langa ndinaona zithunzithunzi ndi masomphenya zimene zinandichititsa mantha.+ 6 Choncho ndinalamula kuti amuna onse anzeru a mʼBabulo awabweretse kwa ine kuti adzandimasulire malotowo.+

7 Pa nthawi imeneyo ansembe ochita zamatsenga, anthu olankhula ndi mizimu, Akasidi* ndi okhulupirira nyenyezi+ anabwera kwa ine. Nditawafotokozera malotowo, sanathe kundiuza kumasulira kwake.+ 8 Kenako Danieli, amene ndinamupatsa dzina lakuti Belitesazara+ potengera dzina la mulungu wanga,+ amenenso mwa iye muli mzimu wa milungu yoyera,+ anabwera kwa ine ndipo ndinamuuza malotowo kuti:

9 ‘Iwe Belitesazara mkulu wa ansembe ochita zamatsenga,+ ndikudziwa bwino kuti mzimu wa milungu yoyera uli mwa iwe+ ndipo palibe chinsinsi chimene ndi chovuta kwambiri kwa iwe.+ Choncho ndiuze zinthu zimene ndinaona mʼmaloto anga komanso kumasulira kwake.

10 Ine nditagona pabedi langa ndinaona masomphenya. Ndinaona mtengo+ wautali kwambiri uli pakati pa dziko lapansi.+ 11 Mtengowo unakula ndipo unakhala wamphamvu kwambiri. Nsonga yake inafika kumwamba ndipo umaonekera mpaka kumalekezero a dziko lonse lapansi. 12 Masamba ake anali okongola ndipo unali ndi zipatso zambiri, moti anthu ndi nyama ankapezamo chakudya chokwanira. Nyama zakutchire zinkakhala mumthunzi wake ndipo mbalame zamumlengalenga zinkakhala munthambi zake. Zamoyo zonse zinkapeza chakudya mumtengowo.

13 Ndikuona masomphenyawo ndili pabedi langa, ndinaona mlonda, mthenga woyera akutsika kuchokera kumwamba.+ 14 Mlondayo analankhula mofuula kuti: “Gwetsani mtengowo+ ndipo mudule nthambi zake. Yoyolani masamba ake ndipo mumwaze zipatso zake. Nyama zithawe pansi pake ndipo mbalame zichoke panthambi zake. 15 Koma musiye chitsa ndi mizu yake munthaka ndipo muchikulunge ndi mkombero wachitsulo komanso wakopa.* Chikhale pakati pa udzu wakutchire ndipo chizinyowa ndi mame akumwamba. Chikhalenso pakati pa nyama zakutchire ndi udzu wapadziko lapansi.+ 16 Mtima wake usinthidwe kuchoka kumtima wa munthu nʼkukhala mtima wa nyama ndipo padutse+ nthawi zokwana 7.+ 17 Alonda ndi amene alamula zimenezi.+ Amithenga oyera ndi amene apempha zimenezi nʼcholinga chakuti anthu adziwe kuti Mulungu Wamʼmwambamwamba ndi Wolamulira wa maufumu a anthu,+ ndiponso adziwe kuti iye amapereka ulamuliro kwa aliyense amene akufuna kumupatsa ndipo amaika ngakhale munthu wonyozeka kwambiri kuti azilamulira.”

18 Amenewa ndi maloto amene ine Mfumu Nebukadinezara ndinalota. Tsopano iwe Belitesazara umasulire malotowa, chifukwa amuna ena onse anzeru a mu ufumu wanga alephera kundiuza kumasulira kwake.+ Koma iwe ungathe kuwamasulira chifukwa mzimu wa milungu yoyera uli mwa iwe.’

19 Pa nthawi imeneyo Danieli, amene dzina lake ndi Belitesazara,+ anada nkhawa kwa kanthawi ndipo anachita mantha.

Mfumuyo inamuuza kuti, ‘Iwe Belitesazara, usachite mantha ndi malotowa komanso kumasulira kwake.’

Belitesazara anayankha kuti, ‘Inu mbuyanga, zikanakhala bwino malotowa akanakhala okhudza anthu amene amadana nanu. Zikanakhalanso bwino kumasulira kwake kukanakhala kokhudza adani anu.

20 Inu munaona mtengo umene unakula kwambiri ndipo unakhala wamphamvu. Nsonga ya mtengowo inakafika mpaka kumwamba ndipo unkaoneka padziko lonse lapansi.+ 21 Masamba ake anali okongola ndipo unali ndi zipatso zambiri. Mumtengomo munali zakudya zokwanira anthu ndi nyama zonse. Nyama zakutchire zinkakhala pansi pake ndipo mbalame zamumlengalenga zinkakhala munthambi zake.+ 22 Mtengowo ndi inuyo mfumu, chifukwa mwakula ndipo mwakhala wamphamvu. Ulemerero wanu wakula mpaka kukafika kumwamba+ ndipo ulamuliro wanu wafika kumalekezero a dziko lapansi.+

23 Ndiyeno inu mfumu munaona mlonda,+ mthenga woyera akutsika kuchokera kumwamba, ndipo ankanena kuti: “Gwetsani mtengowo ndipo muuwononge, koma musiye chitsa ndi mizu yake munthaka ndipo muchikulunge ndi mkombero wachitsulo ndi wakopa.* Chitsacho chikhale pakati pa udzu wakutchire ndipo chizinyowa ndi mame akumwamba. Chizikhala limodzi ndi nyama zakutchire mpaka patadutsa nthawi zokwana 7.”+ 24 Kumasulira kwake ndi kumeneku inu mfumu. Zimene zidzakuchitikireni inu mbuyanga mfumu ndi lamulo la Mulungu Wamʼmwambamwamba. 25 Inuyo adzakuthamangitsani pakati pa anthu ndipo muzidzakhala ndi nyama zakutchire. Muzidzadya udzu ngati ngʼombe ndipo muzidzanyowa ndi mame akumwamba.+ Ndiyeno padzadutsa+ nthawi zokwana 7+ mpaka mutadziwa kuti Mulungu Wamʼmwambamwamba ndi Wolamulira wa maufumu a anthu ndiponso kuti amapereka ulamuliro kwa aliyense amene akufuna kumupatsa.+

26 Koma chifukwa ananena kuti asiye chitsa cha mtengowo ndi mizu yake,+ inu mudzayambiranso kulamulira mu ufumu wanu mutadziwa kuti Mulungu ndi amene akulamulira kumwamba. 27 Choncho inu mfumu, mverani malangizo anga. Musiye kuchita machimo ndipo muzichita zinthu zabwino. Musiyenso kuchita zinthu zoipa ndipo muzichitira chifundo anthu osauka. Mukatero, mwina zinthu zidzapitiriza kukuyenderani bwino kwa nthawi yaitali.’”+

28 Zonsezi zinachitikiradi Mfumu Nebukadinezara.

29 Patapita miyezi 12 Nebukadinezara ankayenda padenga la nyumba yachifumu ya ku Babulo. 30 Mfumuyo inkanena kuti: “Kodi uyu si Babulo Wamkulu amene ine ndamanga ndi mphamvu zanga zazikulu kuti kukhale nyumba yachifumu nʼcholinga choti ulemerero wa ufumu wanga uonekere?”

31 Mfumuyo ili mkati molankhula mawu amenewa, kumwamba kunamveka mawu akuti: “Tamvera iwe Mfumu Nebukadinezara! ‘Ufumu wachoka mʼmanja mwako,+ 32 ndipo akuthamangitsa pakati pa anthu. Uzikhala ndi nyama zakutchire ndipo uzidya udzu ngati ngʼombe. Ndiyeno padutsa nthawi zokwana 7 mpaka utadziwa kuti Mulungu Wamʼmwambamwamba ndi Wolamulira wa maufumu a anthu, ndiponso kuti amapereka ulamuliro kwa aliyense amene akufuna kumupatsa.’”+

33 Nthawi yomweyo mawuwa anakwaniritsidwa pa Nebukadinezara. Iye anathamangitsidwa pakati pa anthu ndipo anayamba kudya udzu ngati ngʼombe komanso thupi lake linkanyowa ndi mame akumwamba. Tsitsi lake linatalika kwambiri ngati nthenga za chiwombankhanga ndipo zikhadabo zake zinatalika ngati za mbalame.+

34 “Nthawi imeneyi itatha,+ ine Nebukadinezara ndinayangʼana kumwamba ndipo nzeru zanga zinabwerera. Ndinatamanda Wamʼmwambamwamba ndipo amene adzakhalepo mpaka kalekale ndinamutamanda ndi kumulemekeza, chifukwa ulamuliro wake udzakhalapo mpaka kalekale ndipo ufumu wake udzakhalapo kumibadwomibadwo.+ 35 Anthu onse okhala padziko lapansi ndi opanda pake poyerekezera ndi Mulungu. Iye amachita zinthu mogwirizana ndi zofuna zake pakati pa magulu akumwamba ndi anthu okhala padziko lapansi. Palibe aliyense amene angamulepheretse kuchita zimene akufuna+ kapena kumufunsa kuti, ‘Mukuchita chiyani?’+

36 Pa nthawi imeneyo nzeru zanga zinabwerera ndipo ndinalandiranso ufumu wanga ndi ulemerero wake wonse komanso ulemu.+ Nduna zanga zikuluzikulu ndi anthu olemekezeka anayamba kufunsiranso malangizo kwa ine. Ndinabwezeretsedwa pampando wanga wachifumu ndipo anthu anayamba kundipatsa ulemu waukulu.

37 Tsopano ine Nebukadinezara ndikutamanda, kukweza ndi kulemekeza Mfumu yakumwamba,+ chifukwa ntchito zake zonse ndi zogwirizana ndi choonadi, njira zake ndi zolungama+ ndiponso amatha kutsitsa anthu onyada.”+

5 Pa nthawi imene Belisazara+ anali mfumu anakonzera nduna zake 1,000 phwando lalikulu ndipo iyeyo ankamwa vinyo atakhala patsogolo pawo.+ 2 Belisazara ataledzera ndi vinyoyo analamula kuti abweretse ziwiya zagolide ndi zasiliva zimene Nebukadinezara bambo ake anatenga mʼkachisi ku Yerusalemu.+ Anachita zimenezi kuti mfumuyo, nduna zake, adzakazi* ake ndi akazi ake ena amweremo. 3 Ndiyeno anabweretsa ziwiya zagolide zimene anazitenga mʼkachisi, mʼnyumba ya Mulungu ku Yerusalemu. Kenako mfumuyo, nduna zake, adzakazi ake ndi akazi ake ena anayamba kumwera mʼziwiyazo. 4 Iwo anamwa vinyo nʼkuyamba kutamanda milungu yagolide, yasiliva, yakopa,* yachitsulo, yamitengo ndi yamiyala.

5 Nthawi yomweyo, dzanja la munthu linaonekera ndipo linayamba kulemba pakhoma lapulasitala la nyumba ya mfumu, pafupi ndi choikapo nyale ndipo mfumuyo inaona dzanja limene linkalembalo. 6 Ndiyeno nkhope ya mfumuyo inasintha ndipo iye anachita mantha kwambiri. Miyendo komanso mawondo+ ake anayamba kunjenjemera.

7 Ndiye mfumuyo inaitana mofuula olankhula ndi mizimu, Akasidi* ndi okhulupirira nyenyezi.+ Mfumuyo inauza amuna anzeru a mʼBabulo amenewa kuti: “Aliyense amene angawerenge mawuwa nʼkundiuza kumasulira kwake, ndimuveka zovala zapepo ndi mkanda wagolide mʼkhosi+ ndipo akhala wolamulira wachitatu mu ufumuwu.”+

8 Amuna onse anzeru anabwera kwa mfumu koma sanathe kuwerenga mawu amene analembedwawo kapena kuuza mfumu kumasulira kwake.+ 9 Choncho Mfumu Belisazara inachita mantha kwambiri ndipo nkhope yake inasintha. Nduna zakenso zinathedwa nzeru.+

10 Mfumukazi itamva mawu a mfumu ndi a nduna zake, inalowa mʼchipinda chimene ankachitira phwandolo. Mfumukaziyo inati: “Inu mfumu, mukhale ndi moyo mpaka kalekale. Musachite mantha komanso nkhope yanu isasinthe. 11 Mu ufumu wanu muli munthu amene ali ndi mzimu wa milungu yoyera. Mʼmasiku a bambo anu, anthu anazindikira kuti munthuyu ndi wodziwa zinthu kwambiri, wozindikira ndiponso ali ndi nzeru zofanana ndi nzeru za milungu.+ Ndiyeno bambo anu, Mfumu Nebukadinezara, anamuika kuti akhale mkulu wa ansembe ochita zamatsenga, anthu okhulupirira mizimu, Akasidi* ndi anthu okhulupirira nyenyezi.+ Ndithudi mfumu, bambo anu anamupatsa udindo umenewu. 12 Anachita zimenezi chifukwa Danieli, amene mfumu inamupatsa dzina lakuti Belitesazara,+ anali ndi luso lodabwitsa, anali wodziwa zinthu ndi wozindikira pa nkhani yomasulira maloto, kumasulira mikuluwiko komanso kuthana ndi zinthu zovuta.*+ Tsopano itanani Danieli ndipo akuuzani kumasulira kwa mawu amenewa.”

13 Choncho anabweretsa Danieli kwa mfumu ndipo mfumuyo inamufunsa kuti: “Kodi iwe ndiwe Danieli, mmodzi wa anthu amene anatengedwa ukapolo ku Yuda ndi bambo anga mfumu?+ 14 Ndamva kuti mwa iwe muli mzimu wa milungu+ ndiponso kuti uli ndi luso lodabwitsa, ndiwe wozindikira komanso kuti uli ndi nzeru zodabwitsa.+ 15 Ineyo anandibweretsera amuna anzeru ndi anthu okhulupirira mizimu kuti awerenge mawu amene alembedwawa nʼkundiuza kumasulira kwake, koma iwo alephera kumasulira uthenga wake.+ 16 Koma ndamva kuti iweyo umatha kumasulira zinthu+ komanso kuthana ndi zinthu zovuta.* Ndiye ngati ungathe kuwerenga mawuwa nʼkundiuza kumasulira kwake, ndikuveka zovala zapepo ndi mkanda wagolide mʼkhosi mwako ndipo ukhala wolamulira wachitatu mu ufumuwu.”+

17 Ndiyeno Danieli anayankha mfumuyo kuti: “Mphatso zanuzo mukhoza kusunga ndipo mphoto zanuzo mupatse ena. Komabe, inu mfumu, ndikuwerengerani mawu amene alembedwawa ndipo ndikuuzani kumasulira kwake. 18 Inu mfumu, Mulungu Wamʼmwambamwamba anapatsa bambo anu Nebukadinezara ufumu, ukulu, ulemu ndi ulemerero.+ 19 Chifukwa chakuti Mulungu anamupatsa ukulu umenewu, anthu a mitundu yonse komanso anthu olankhula zinenero zosiyanasiyana ankanjenjemera chifukwa cha mantha pamaso pake.+ Aliyense amene ankafuna kumupha ankamupha, amene ankafuna kumusiya ndi moyo ankamusiya ndipo aliyense amene ankafuna kumukweza ankamukweza, amene ankafuna kumutsitsa ankamutsitsa.+ 20 Koma pamene mtima wake unayamba kudzikuza ndiponso pamene anaumitsa mtima wake nʼkuchita zinthu modzikweza,+ anatsitsidwa pampando wake wachifumu ndipo ulemerero wake unachotsedwa. 21 Iye anathamangitsidwa pakati pa anthu ndipo mtima wake unasinthidwa nʼkukhala ngati wa nyama moti anayamba kukhala limodzi ndi abulu akutchire. Iye ankadya udzu ngati ngʼombe ndipo thupi lake linkanyowa ndi mame akumwamba, mpaka pamene anadziwa kuti Mulungu Wamʼmwambamwamba ndi Wolamulira wa maufumu a anthu ndiponso kuti amapereka ulamuliro kwa munthu aliyense amene akufuna kumupatsa.+

22 Koma inuyo a Belisazara, amene ndinu mwana wake, simunadzichepetse mumtima mwanu ngakhale kuti mukudziwa zonsezi. 23 Mʼmalomwake mwadzikweza pamaso pa Ambuye wakumwamba+ ndipo munalamula anthu kuti akubweretsereni ziwiya zamʼnyumba yake.+ Ndiyeno inuyo, nduna zanu, adzakazi anu ndi akazi anu ena mwamwera vinyo mʼziwiya zimenezi ndipo mwatamanda milungu yasiliva, yagolide, yakopa, yachitsulo, yamitengo ndi yamiyala imene siona, kumva kapena kudziwa chilichonse.+ Koma Mulungu amene amakupatsani mpweya komanso amene ali ndi mphamvu zolamulira moyo wanu, simunamulemekeze.+ 24 Choncho Mulungu watumiza dzanja limene lalemba mawu amenewa.+ 25 Mawu amene alembedwa ndi awa: MENE, MENE, TEKELI ndi PARASINI.

26 Kumasulira kwa mawuwa ndi uku: MENE, Mulungu wawerenga masiku a ufumu wanu ndipo wauthetsa.+

27 TEKELI, mwayezedwa pasikelo ndipo mwapezeka kuti mukuperewera.

28 PERESI, ufumu wanu wagawidwa ndipo waperekedwa kwa Amedi ndi Aperisiya.”+

29 Ndiyeno Belisazara analamula kuti Danieli avekedwe zovala zapepo ndi mkanda wagolide mʼkhosi mwake. Ndipo analengeza kuti Danieli akhala wolamulira wachitatu mu ufumuwo.+

30 Usiku womwewo, Belisazara mfumu ya Akasidi anaphedwa.+ 31 Dariyo+ Mmedi anapatsidwa ufumuwo ndipo anali ndi zaka pafupifupi 62.

6 Ndiyeno Dariyo anaona kuti ndi bwino kuti aike masatarapi* 120 oti aziyangʼanira zigawo zonse za ufumu wake.+ 2 Anaikanso nduna zapamwamba zitatu kuti ziziyangʼanira masatarapiwo ndipo Danieli anali mmodzi wa ndunazo.+ Masatarapiwo+ ankayenera kuuza nduna zimenezi chilichonse chimene chikuchitika nʼcholinga chakuti zinthu za mfumu zisawonongeke. 3 Ndiyeno Danieli anaonetsa kuti anali wodziwa kugwira ntchito bwino kuposa nduna zina zapamwamba ndi masatarapi, chifukwa anali ndi luso lodabwitsa+ ndipo mfumu inaganiza zomukweza kuti akhale ndi udindo waukulu mu ufumu wonsewo.

4 Pa nthawiyo, nduna zapamwamba ndi masatarapi aja ankafufuza zifukwa zoti amuimbire mlandu Danieli pa nkhani zokhudza mmene ankayendetsera zinthu mu ufumuwo. Koma iwo sanapeze chifukwa chilichonse chomuimbira mlandu kapena chinthu chilichonse chachinyengo chimene anachita. Zinali choncho chifukwa Danieli anali wokhulupirika ndipo iwo anapeza kuti sankanyalanyaza udindo wake kapena kuchita zachinyengo zilizonse. 5 Choncho amuna amenewa anati: “Danieliyu sitimupezera chifukwa chilichonse. Ngati tikufuna kumupezera chifukwa, chikhale chokhudzana ndi lamulo la Mulungu wake.”+

6 Choncho nduna zapamwamba zimenezi ndi masatarapi aja anapita kwa mfumu ali chigulu ndipo anauza mfumuyo kuti: “Inu Mfumu Dariyo, mukhale ndi moyo mpaka kalekale. 7 Nduna zonse zapamwamba za mu ufumu uno, akuluakulu a boma, masatarapi, alangizi a mfumu ndi abwanamkubwa agwirizana kuti inu mfumu mukhazikitse lamulo loletsa munthu aliyense kupemphera kwa mulungu kapena kwa munthu wina aliyense kwa masiku 30, kupatulapo kwa inu nokha mfumu. Aliyense amene samvera lamulo limeneli aponyedwe mʼdzenje la mikango.+ 8 Ndiyeno inu mfumu khazikitsani lamulo ndipo musaine+ kuti lamulolo lisasinthe, mogwirizana ndi malamulo a Amedi ndi Aperisiya, amene sangasinthidwe.”+

9 Choncho Mfumu Dariyo inasainira lamulo loletsa kupempheralo.

10 Koma Danieli atangodziwa kuti lamulo limeneli lasainidwa, anapita kunyumba kwake. Mawindo a chipinda chake chamʼmwamba anali otsegula ndipo anayangʼana ku Yerusalemu.+ Katatu pa tsiku, iye ankagwada nʼkupemphera kwa Mulungu wake komanso kumutamanda, ngati mmene ankachitira nthawi zonse lamuloli lisanasainidwe. 11 Pa nthawi imeneyo, amuna amenewa analowa mʼnyumbamo ali chigulu ndipo anapeza Danieli akuchonderera ndi kupempha Mulungu wake kuti amukomere mtima.

12 Choncho anapita kwa mfumu kukaikumbutsa za lamulo limene inakhazikitsa lija. Iwo anati: “Kodi inu mfumu, si paja munasainira lamulo lonena kuti kwa masiku 30 munthu aliyense amene angapezeke akupemphera kwa mulungu kapena kwa munthu wina aliyense, kupatulapo kwa inu nokha, aponyedwe mʼdzenje la mikango?” Mfumuyo inayankha kuti: “Nkhani imeneyi ndi yodziwika bwino, mogwirizana ndi malamulo a Amedi ndi Aperisiya, amene sangasinthidwe.”+ 13 Nthawi yomweyo iwo anauza mfumuyo kuti: “Danieli, mmodzi wa anthu amene anatengedwa ukapolo ku Yuda,+ sakukumverani inu mfumu kapena kumvera lamulo limene munasainira koma akumapemphera katatu pa tsiku.”+ 14 Mfumu itangomva zimenezi inakhumudwa kwambiri ndipo inayamba kuganiza zimene ingachite kuti ipulumutse Danieli. Mfumuyo inayesetsa kufunafuna njira yoti imupulumutsire mpaka dzuwa linalowa. 15 Pamapeto pake, amuna amenewa anapita kwa mfumu ali chigulu ndipo anaiuza kuti: “Inu mfumu, mukudziwa kuti malamulo a Amedi ndi Aperisiya amanena kuti lamulo lililonse lokhazikitsidwa ndi mfumu silingasinthidwe.”+

16 Choncho mfumuyo inalamula kuti abweretse Danieli. Atabwera naye anamuponya mʼdzenje la mikango.+ Koma mfumu inauza Danieli kuti: “Mulungu wako amene ukumutumikira mosalekeza akupulumutsa.” 17 Ndiyeno anabweretsa mwala nʼkutseka pakhomo la* dzenjelo. Kenako mfumu inadinda mwalawo ndi mphete yake yodindira ndipo nduna zakenso zinaudinda ndi mphete yawo yodindira, kuti chilichonse chokhudza Danieli chisasinthidwe.

18 Kenako mfumu inapita kunyumba yake yachifumu. Usiku umenewo mfumuyo inasala kudya ndipo inakana zosangalatsa zilizonse* komanso sinathe kugona.* 19 Ndiyeno kutangoyamba kuwala mʼbandakucha, mfumuyo inadzuka ndipo inapita mofulumira kudzenje la mikango lija. 20 Itayandikira dzenjelo, inaitana Danieli ndi mawu achisoni. Mfumuyo inafunsa Danieli kuti: “Danieli mtumiki wa Mulungu wamoyo, kodi Mulungu wako amene umamutumikira mosalekeza wakupulumutsa kwa mikango?” 21 Nthawi yomweyo Danieli anayankha mfumuyo kuti: “Inu mfumu, mukhale ndi moyo mpaka kalekale. 22 Mulungu wanga watumiza mngelo wake kudzatseka pakamwa pa mikango+ moti sinandivulaze,+ chifukwa iye sanandipeze ndi mlandu uliwonse ndipo inunso mfumu sindinakulakwireni chilichonse.”

23 Mfumu inasangalala kwambiri ndipo inalamula kuti Danieli amutulutse mʼdzenjemo. Danieli anatulutsidwadi mʼdzenjemo ndipo sanavulale paliponse chifukwa anakhulupirira Mulungu wake.+

24 Kenako mfumu inalamula kuti abweretse amuna amene ananenera Danieli zoipa aja. Atawabweretsa, anawaponya mʼdzenje la mikango pamodzi ndi ana awo komanso akazi awo. Iwo asanafike nʼkomwe pansi pa dzenjelo, mikango inawakhadzulakhadzula nʼkuphwanya mafupa awo onse.+

25 Ndiyeno Mfumu Dariyo inalemba makalata opita kwa anthu a mitundu yonse ndi anthu olankhula zilankhulo zosiyanasiyana okhala padziko lonse lapansi+ kuti: “Mukhale ndi mtendere wochuluka. 26 Ine ndikulamula kuti mʼzigawo zonse za ufumu wanga, anthu azinjenjemera chifukwa cha mantha pamaso pa Mulungu wa Danieli.+ Chifukwa iye ndi Mulungu wamoyo ndipo adzakhalapo mpaka kalekale. Ufumu wake sudzawonongedwa komanso ulamuliro wake udzakhalapo kwamuyaya.+ 27 Iye amapulumutsa+ ndi kulanditsa anthu ake, ndipo amachita zizindikiro komanso zinthu zodabwitsa kumwamba ndi padziko lapansi,+ moti wapulumutsa Danieli kwa mikango.”

28 Choncho zinthu zinamuyendera bwino Danieli mu ufumu wa Dariyo+ ndiponso mu ufumu wa Koresi wa Chiperisiya.+

7 Mʼchaka choyamba cha ulamuliro wa Mfumu Belisazara+ ya Babulo, Danieli analota maloto ndipo anaona masomphenya atagona pabedi lake.+ Ndiyeno analemba zimene analotazo+ ndipo anafotokoza nkhani yonseyo. 2 Iye anati:

“Mʼmasomphenya usiku, ndinaona mphepo 4 zakumwamba zikuvundula nyanja yaikulu.+ 3 Ndipo zilombo 4 zikuluzikulu+ zinatuluka mʼnyanjayo. Chilombo chilichonse chinali chosiyana ndi chinzake.

4 Chilombo choyamba chinali chooneka ngati mkango+ ndipo chinali ndi mapiko a chiwombankhanga.+ Ndinapitiriza kuchiyangʼana mpaka pamene mapiko ake anathotholedwa. Ndiyeno anachitukula panthaka nʼkuchiimiriritsa ndi miyendo iwiri ngati munthu. Kenako anachipatsa mtima wa munthu.

5 Ndinaonanso chilombo china chachiwiri, chooneka ngati chimbalangondo.+ Chinali chotukuka mbali imodzi ndipo mʼkamwa mwake munali nthiti zitatu pakati pa mano ake. Chilombochi chinauzidwa kuti, ‘Nyamuka, idya nyama yambiri.’+

6 Kenako ndinapitiriza kuyangʼana ndipo ndinaona chilombo china chooneka ngati kambuku+ koma chinali ndi mapiko 4 pamsana pake ooneka ngati a mbalame. Chilombochi chinali ndi mitu 4+ ndipo chinapatsidwa ulamuliro.

7 Ndinapitiriza kuona masomphenya usiku umenewo ndipo ndinaona chilombo cha nambala 4. Chilombocho chinali choopsa kwambiri, chochititsa mantha komanso champhamvu kwambiri ndipo chinali ndi mano akuluakulu achitsulo. Chinkadya komanso kuphwanyaphwanya chilichonse chimene chinali nacho pafupi ndipo zotsala chinkazipondaponda ndi mapazi ake.+ Chilombochi chinali chosiyana ndi zilombo zina zonse zimene ndinaona poyamba ndipo chinali ndi nyanga 10. 8 Pa nthawi imene ndimayangʼanitsitsa nyangazo, ndinaona kuti nyanga ina yaingʼono+ yamera pakati pa nyangazo. Nyanga zitatu pa nyangazi zinazulidwa pamalo amene nyanga yaingʼonoyo inamera. Nyangayi inali ndi maso ngati a munthu, ndipo inali ndi pakamwa polankhula mawu odzitukumula.*+

9 Ndinapitiriza kuyangʼana mpaka pamene mipando yachifumu inaikidwa ndipo Wamasiku Ambiri+ anakhala pampando wake wachifumu.+ Zovala zake zinali zoyera kwambiri+ ndipo tsitsi lake linali looneka ngati ubweya wa nkhosa woyera. Mpando wake wachifumu unkaoneka ngati malawi a moto ndipo mawilo a mpandowo ankaoneka ngati moto umene ukuyaka.+ 10 Mtsinje wa moto unkayenda kuchokera kwa iye.+ Panali atumiki okwana 1 miliyoni* amene ankatumikira nthawi zonse ndi atumiki enanso 100 miliyoni* amene ankatumikira pamaso pake nthawi zonse.+ Bwalo la milandu+ linayamba kuzenga mlandu ndipo mabuku anatsegulidwa.

11 Pa nthawi imeneyo, ndinapitirizabe kuyangʼana chifukwa ndinkamva mawu odzitukumula* amene nyanga ija inkalankhula.+ Ndinapitiriza kuyangʼana mpaka pamene chilombocho chinaphedwa ndipo thupi lake linaponyedwa pamoto nʼkuwonongedwa. 12 Koma zilombo zinazo+ anazilanda ulamuliro, ndipo anazilola kuti zikhalebe moyo kwa kanthawi komanso nyengo yoikidwiratu.

13 Ndinapitiriza kuona masomphenya usikuwo ndipo ndinaona winawake wooneka ngati mwana wa munthu+ akubwera mʼmitambo. Iye analoledwa kufika kwa Wamasiku Ambiri+ uja ndipo anamubweretsa pafupi kwambiri ndi Wamasiku Ambiriyo. 14 Kenako anamupatsa ulamuliro,+ ulemu+ ndi ufumu kuti anthu a mitundu yonse komanso anthu olankhula zilankhulo zosiyanasiyana azimutumikira.+ Ulamuliro wake udzakhalapo mpaka kalekale ndipo sudzatha. Ufumu wake sudzawonongedwa.+

15 Koma ineyo Danieli, ndinavutika kwambiri mumtima chifukwa masomphenya amene ndinaona ankandichititsa mantha.+ 16 Ndinayandikira mmodzi mwa amene anaimirira pamenepo kuti ndimufunse tanthauzo la zimenezi. Choncho iye anandifotokozera kumasulira kwa zinthu zimenezi. Iye anati:

17 ‘Zilombo zikuluzikulu zimenezi, zomwe zilipo 4,+ zikuimira mafumu 4 amene adzalamulire padziko lapansi.*+ 18 Koma oyera a Mulungu Wamkulu+ adzalandira ufumu+ ndipo ufumuwo udzakhala wawo+ mpaka kalekale, inde kwamuyaya.’

19 Ndiyeno ndinkafuna kudziwa zambiri zokhudza chilombo cha nambala 4 chija, chimene chinali chosiyana ndi zina zonse. Chilombo chimenechi chinali choopsa kwambiri. Mano ake anali achitsulo, zikhadabo zake zinali zakopa* ndipo chinkadya komanso kuphwanyaphwanya zinthu zimene zinali nacho pafupi. Zotsala chinkazipondaponda ndi mapazi ake.+ 20 Ndinkafunanso kudziwa za nyanga 10+ zimene zinali pamutu pake ndi nyanga ina imene inamera nʼkuchititsa kuti nyanga zitatu zija zigwe.+ Nyanga imeneyi inali ndi maso ndi pakamwa polankhula mawu odzitukumula* ndipo inkaoneka yaikulu kuposa zina zija.

21 Ndinapitirizabe kuyangʼana pamene nyangayo inkachita nkhondo ndi oyera ndipo inkapambana pankhondoyo,+ 22 mpaka pamene Wamasiku Ambiri+ anabwera ndipo anapereka chiweruzo chokomera oyera a Mulungu Wamkulu.+ Ndipo nthawi yomwe inaikidwiratu yoti oyerawo atenge ufumu inakwana.+

23 Ndiyeno iye anandiuza kuti: ‘Ponena za chilombo cha nambala 4 chimenechi, pali ufumu wa nambala 4 umene udzakhalepo padziko lapansi. Udzakhala wosiyana ndi maufumu ena onse ndipo udzadya dziko lonse lapansi komanso udzalipondaponda nʼkuliphwanyaphwanya.+ 24 Ponena za nyanga 10 zija, mu ufumuwo mudzatuluka mafumu 10. Pambuyo pa mafumu amenewa padzatulukanso mfumu ina imene idzakhale yosiyana ndi oyambawa ndipo idzagonjetsa mafumu atatu.+ 25 Idzalankhula mawu otsutsana ndi Mulungu Wamʼmwambamwamba+ ndipo idzapitiriza kuzunza oyera a Mulungu Wamkulu. Idzafuna kuti isinthe nthawi ndi lamulo ndipo oyerawo adzaperekedwa mʼmanja mwake kwa nthawi imodzi, nthawi ziwiri ndi hafu ya nthawi.*+ 26 Koma Bwalo la milandu linayamba kuzenga mlandu ndipo linachotsa ulamuliro wa mfumuyo nʼcholinga choti mfumuyo aiwonongeretu.+

27 Ufumu, ulamuliro, ndi ulemerero wa maufumu apadziko lonse lapansi zinaperekedwa kwa anthu amene ndi oyera a Mulungu Wamkulu.+ Ufumu wawo udzakhalapo mpaka kalekale+ ndipo maulamuliro onse adzawatumikira ndi kuwamvera.’

28 Nkhani imeneyi yathera pamenepa. Ineyo Danieli, ndinachita mantha kwambiri moti nkhope yanga inasintha. Koma nkhaniyi ndinaisunga mumtima mwanga.”

8 Mʼchaka chachitatu cha ulamuliro wa Mfumu Belisazara,+ ineyo Danieli ndinaona masomphenya pambuyo pa masomphenya amene ndinaona poyamba aja.+ 2 Ndikuona masomphenyawo ndinapezeka kuti ndili kunyumba yachifumu* ku Susani,+ imene ili mʼchigawo cha Elamu.+ Ndinaona masomphenyawa kuti ndinali mʼmphepete mwa mtsinje wa Ulai. 3 Nditayangʼana ndinaona nkhosa yamphongo+ itaima pafupi ndi mtsinjewo ndipo inali ndi nyanga ziwiri.+ Nyanga ziwirizi zinali zazitali koma imodzi, imene inamera pomalizira, inali yaitali kuposa inzake.+ 4 Ndinaona nkhosa yamphongoyo ikuukira adani ake kumadzulo, kumpoto ndi kumʼmwera ndipo palibe zilombo zakutchire zimene zinalimbana nayo komanso palibe amene akanakwanitsa kupulumutsa aliyense ku mphamvu zake.*+ Nkhosayo inkachita zofuna zake ndipo inkadzitama kwambiri.

5 Ndikupitiriza kuyangʼana, ndinaona mbuzi yamphongo+ ikuchokera kumadzulo* kudutsa padziko lonse lapansi koma sinkaponda pansi. Pakati pa maso a mbuziyo panali nyanga yoonekera patali.+ 6 Mbuziyo inkabwera kumene kunali nkhosa yamphongo ya nyanga ziwiri ija, imene ndinaiona itaima pafupi ndi mtsinje. Inkathamangira kumene kunali nkhosayo itakwiya kwambiri.

7 Ndinaona mbuziyo ikufika pafupi kwambiri ndi nkhosa yamphongoyo ndipo inakwiyira kwambiri nkhosayo. Kenako inagunda nkhosayo nʼkuthyola nyanga zake ziwiri, ndipo nkhosayo inalibe mphamvu zotha kulimbana nayo. Mbuziyo inagwetsera pansi nkhosayo nʼkuipondaponda ndipo panalibe woti aipulumutse ku mphamvu za* mbuziyo.

8 Kenako mbuzi yamphongoyo inayamba kudzitukumula mopitirira muyezo. Koma itangokhala yamphamvu, nyanga yake yaikulu inathyoledwa. Pamene panali nyangayo panamera nyanga 4 zoonekera patali ndipo zinaloza kumphepo 4 zakumwamba.+

9 Imodzi mwa nyanga zimenezi inatulutsa nyanga ina yaingʼono ndipo mphamvu zake zinachuluka kwambiri moti zinafika kumʼmwera, kumʼmawa* ndi ku Dziko Lokongola.+ 10 Inakula kwambiri mpaka inakafika kwa gulu lakumwamba, moti inachititsa kuti ena amʼgululi komanso nyenyezi zina zigwere padziko lapansi ndipo inazipondaponda. 11 Nyangayo inadzitukumula ngakhale pamaso pa Kalonga wa gululo. Inachititsa kuti nsembe imene inkaperekedwa nthawi zonse kwa Kalongayo isamaperekedwenso ndipo malo opatulika amene iye anakhazikitsa anagwetsedwa.+ 12 Chifukwa cha uchimo, gulu lakumwamba lija limodzi ndi nsembe imene inkaperekedwa nthawi zonse zinaperekedwa kwa nyangayo ndipo inapitiriza kugwetsera choonadi pansi. Nyangayo inkachita zofuna zake ndipo inapambana.

13 Ndiyeno ndinamva mngelo akulankhula ndipo mngelo wina anafunsa mngelo amene ankalankhulayo kuti: “Kodi masomphenya okhudza nsembe imene inkaperekedwa nthawi zonse komanso tchimo lobweretsa chiwonongeko apitiriza kuchitika kwa nthawi yaitali bwanji+ nʼkumachititsa kuti malo opatulika komanso gululo lizipondedwapondedwa?” 14 Iye anandiuza kuti: “Mpaka nsembe za tsiku ndi tsiku zokwana 2,300, zamadzulo ndi zamʼmawa, zitadutsa. Kenako malo opatulika adzakonzedwanso kuti akhale ngati mmene analili poyamba.”

15 Ndiyeno pamene ineyo Danieli ndinkaona masomphenyawo nʼkumawaganizira kuti ndiwamvetse, mwadzidzidzi ndinaona winawake wooneka ngati munthu ataima patsogolo panga. 16 Kenako ndinamva mawu a munthu kuchokera pakati pa mtsinje wa Ulai.+ Iye anaitana kuti: “Gabirieli,+ munthuyo umuthandize kuti amvetsetse zimene waona.”+ 17 Choncho iye anabwera pafupi ndi pamene ine ndinaima. Koma atafika, ndinachita mantha kwambiri ndipo ndinagwada nʼkuwerama mpaka nkhope yanga pansi. Ndiyeno anandiuza kuti: “Iwe mwana wa munthu, dziwa kuti masomphenyawa ndi okhudza nthawi yamapeto.”+ 18 Koma akulankhula nane, ndinagona pansi chafufumimba nʼkugona tulo tofa nato. Ndiyeno iye anandigwira nʼkundiimiritsa pamalo omwe ndinaima aja.+ 19 Kenako anandiuza kuti: “Ine ndikudziwitsa zimene zidzachitike kumapeto kwa nthawi yopereka chiweruzo, chifukwa masomphenyawo adzakwaniritsidwa pa nthawi yoikidwiratu yamapeto.+

20 Nkhosa yamphongo ya nyanga ziwiri imene unaona, ikuimira mfumu ya Mediya ndi mfumu ya Perisiya.+ 21 Mbuzi yamphongo yaubweya wambiri ikuimira mfumu ya Girisi,+ ndipo nyanga yaikulu imene inali pakati pa maso ake ikuimira mfumu yoyamba.+ 22 Koma nyanga imene inathyoka ija ndipo mʼmalomwake nʼkumera zina 4,+ zikuimira maufumu 4 ochokera mu mtundu wake amene adzalamulire, koma sadzakhala ndi mphamvu ngati zake.

23 Kumapeto kwa ufumu wawo, zochita za anthu ochimwawo zikadzafika pachimake, mfumu yooneka mochititsa mantha ndiponso yomvetsa zinthu zovuta kumva idzayamba kulamulira. 24 Mphamvu za mfumuyo zidzachuluka, koma si iye amene adzachititse zimenezi. Idzawononga zinthu zambiri moti idzadabwitsa anthu. Chilichonse chimene mfumuyo izidzachita chizidzaiyendera bwino. Idzawononga anthu amphamvu ndi anthu oyera.+ 25 Mochenjera idzachita zinthu mwachinyengo kuti zinthu ziiyendere bwino ndipo idzadzitukumula kwambiri mumtima mwake. Pa nthawi yamtendere* idzawononga anthu ambiri. Mfumuyo idzalimbana ngakhale ndi Kalonga wa akalonga, koma idzathyoledwa osati ndi dzanja la munthu.

26 Zinthu zimene zanenedwa mʼmasomphenya zokhudza nsembe zamadzulo ndi zamʼmawa zija ndi zoona. Koma iweyo usunge masomphenyawo mwachinsinsi, chifukwa akunena zimene zidzachitike mʼtsogolo patapita masiku ambiri.”+

27 Ndiyeno ineyo Danieli ndinatopa kwambiri ndipo ndinadwala kwa masiku angapo.+ Kenako ndinadzuka nʼkugwira ntchito imene mfumu inandipatsa.+ Koma ndinadabwa kwambiri ndi zimene ndinaona ndipo palibe amene akanazimvetsa.+

9 Mʼchaka choyamba cha Dariyo+ mwana wa Ahasiwero, wa mtundu wa Amedi, amene anaikidwa kuti akhale mfumu ya ufumu wa Akasidi,+ 2 mʼchaka choyamba cha ulamuliro wake, ineyo Danieli ndinazindikira chiwerengero cha zaka zimene zinatchulidwa mʼmawu amene Yehova anauza mneneri Yeremiya, kuti Yerusalemu adzakhala bwinja+ kwa zaka 70.+ Ndinazindikira zimenezi nditawerenga mʼmabuku.* 3 Choncho ndinayangʼana kwa Yehova Mulungu woona ndipo ndinapemphera momuchonderera, ndinasala kudya,+ ndinavala ziguduli komanso kudzithira phulusa. 4 Ndinapemphera kwa Yehova Mulungu wanga nʼkuvomereza machimo athu kuti:

“Inu Yehova Mulungu woona, Mulungu wamkulu komanso wochititsa mantha. Inu mumakwaniritsa pangano lanu ndipo mumasonyeza chikondi chokhulupirika+ kwa anthu amene amakukondani ndi kusunga malamulo anu.+ 5 Ife tachimwa, tachita zinthu zolakwika komanso zoipa ndipo takupandukirani.+ Tapatuka nʼkusiya kutsatira malamulo ndi zigamulo zanu. 6 Sitinamvere atumiki anu aneneri,+ amene analankhula mʼdzina lanu kwa mafumu athu, akalonga athu, makolo athu ndi anthu onse amʼdziko lathu. 7 Inu Yehova ndinu wolungama, koma ifeyo tadzibweretsera manyazi* ngati mmene zilili lero. Manyazi agwira amuna a mu Yuda, anthu a ku Yerusalemu ndi anthu onse a ku Isiraeli, amene ali pafupi ndiponso amene ali kutali, kumayiko onse amene munawabalalitsirako chifukwa choti anakuchitirani zinthu zosakhulupirika.+

8 Inu Yehova, tachita zinthu zochititsa manyazi,* mofanana ndi mafumu athu, akalonga athu ndi makolo athu chifukwa takuchimwirani. 9 Inu Yehova Mulungu wathu, ndinu wachifundo ndi wokhululuka,+ koma ife takupandukirani.+ 10 Sitinamvere mawu anu, inu Yehova Mulungu wathu, chifukwa sitinatsatire malamulo anu amene munatipatsa kudzera mwa atumiki anu, aneneri.+ 11 Aisiraeli onse aphwanya Chilamulo chanu ndipo apatuka posamvera mawu anu. Choncho inu mwatitsanulira temberero ndi malumbiro amene analembedwa mʼChilamulo cha Mose, mtumiki wanu,+ chifukwa takuchimwirani. 12 Inu mwachitadi zimene munachenjeza kuti mudzachitira ifeyo+ ndi atsogoleri athu amene ankatilamulira.* Mwachita zimenezi potigwetsera tsoka lalikulu. Zimene zachitika mu Yerusalemu sizinayambe zachitikapo padziko lonse lapansi.+ 13 Mogwirizana ndi zimene zinalembedwa mʼChilamulo cha Mose, masoka onsewa atigwera.+ Koma sitinapemphe inu Yehova Mulungu wathu kuti mutikomere mtima.* Sitinachite zimenezi posiya zolakwa zathu+ komanso posonyeza kuti tikumvetsa choonadi chanu.*

14 Koma inu Yehova, munakhala tcheru ndipo munatigwetsera tsoka chifukwa inu Yehova Mulungu wathu ndinu wolungama pa ntchito zonse zimene mwachita, koma ife sitinamvere mawu anu.+

15 Tsopano inu Yehova Mulungu wathu, amene munatulutsa anthu anu mʼdziko la Iguputo ndi dzanja lamphamvu+ nʼkuchititsa kuti dzina lanu lidziwike bwino mpaka lero,+ ife tachimwa ndipo tachita zinthu zoipa. 16 Inu Yehova, nthawi zonse mumachita zinthu zolungama.+ Chonde, chotsani mkwiyo wanu waukulu pa Yerusalemu, phiri lanu loyera. Chifukwa cha machimo athu ndi zolakwa za makolo athu, Yerusalemu komanso anthu anu, tikunyozedwa ndi anthu onse otizungulira.+ 17 Tsopano inu Mulungu wathu, imvani pemphero langa ine mtumiki wanu ndi kuchonderera kwanga. Malo anu opatulika+ amene awonongedwa+ akomereni mtima, inu Yehova, chifukwa cha dzina lanu. 18 Inu Mulungu wanga, tcherani khutu lanu kuti mumve. Tsegulani maso anu kuti muone zimene zatichitikira komanso mmene mzinda wodziwika ndi dzina lanu wawonongekera. Ifeyo sitikukuchondererani chifukwa choti tachita zinthu zolungama ayi, koma chifukwa cha chifundo chanu chachikulu.+ 19 Imvani, inu Yehova. Tikhululukireni,+ inu Yehova. Timvereni ndipo muchitepo kanthu, inu Yehova! Musazengereze inu Mulungu wanga, chifukwa cha dzina lanu. Chifukwa mzinda wanu ndi anthu anu amadziwika ndi dzina lanu.”+

20 Ndili mkati molankhula, kupemphera ndi kuvomereza machimo anga ndi machimo a anthu a mtundu wanga, Aisiraeli komanso kupempha Yehova Mulungu wanga kuti andikomere mtima pa nkhani yokhudza phiri loyera la Mulungu wanga,+ 21 inde, ndili mkati molankhula zimenezi mʼpemphero, munthu uja Gabirieli,+ amene ndinamuona mʼmasomphenya poyamba paja,+ anabwera kwa ine nditatopa kwambiri, pa nthawi yopereka nsembe yamadzulo imene imaperekedwa ngati mphatso. 22 Iye anandithandiza kuti ndimvetse, ndipo anandiuza kuti:

“Iwe Danieli, tsopano ndabwera kuti ndikupatse nzeru ndi kukuthandiza kumvetsa zinthu zonsezi. 23 Utangoyamba kupemphera Mulungu anandiuza uthenga, ndiye ndabwera kudzakufotokozera uthengawo chifukwa ndiwe munthu wokondedwa kwambiri.*+ Choncho mvetsera mwatcheru zimene ndikufuna kukuuza ndipo umvetse masomphenyawa.

24 Pali milungu* 70 imene yaikidwa yokhudza anthu a mtundu wako ndi mzinda wanu woyera+ ndi cholinga choti athetse kuphwanya malamulo, athetse machimo,+ aphimbe cholakwa,+ abweretse chilungamo kuti chikhalepo mpaka kalekale,+ adinde chidindo pamasomphenya ndi maulosi,*+ ndiponso kuti adzoze Malo Opatulika Koposa.* 25 Uyenera kudziwa ndi kuzindikira kuti kuchokera pamene lamulo lakuti Yerusalemu akonzedwe ndi kumangidwanso+ lidzaperekedwe kukafika pamene Mesiya*+ Mtsogoleri+ adzaonekere, padzadutsa milungu 7 komanso milungu 62.+ Yerusalemu adzakonzedwa ndi kumangidwanso ndipo adzakhala ndi bwalo ndi ngalande yachitetezo. Koma zimenezi zidzachitika pa nthawi ya mavuto.

26 Pambuyo pa milungu 62 imeneyi, Mesiya adzaphedwa+ ndipo sadzasiya kalikonse.+

Mtsogoleri adzabwera ndi gulu lake lankhondo ndipo adzawononga mzindawo ndi malo oyera.+ Malo oyerawo adzafafanizidwa ndi madzi osefukira ndipo padzakhala nkhondo mpaka kumapeto. Mogwirizana ndi zimene Mulungu wasankha, kudzakhala chiwonongeko.+

27 Iye* adzasungira anthu ambiri pangano kwa mlungu umodzi. Ndiye pakatikati pa mlunguwo adzathetsa nsembe zanyama ndi nsembe zina zoperekedwa ngati mphatso.+

Wowonongayo adzabwera pamapiko a zinthu zonyansa ndipo zimene Mulungu wasankha zija zidzakhuthulidwanso pachowonongedwacho+ kufikira chitafafanizidwa.”

10 Mʼchaka chachitatu cha ulamuliro wa Mfumu Koresi+ ya Perisiya, Mulungu anamuululira nkhani inayake Danieli, amene ankadziwikanso ndi dzina lakuti Belitesazara.+ Nkhani imene anauzidwayo inali yoona ndipo inali yokhudza nkhondo yaikulu. Danieli anamvetsa nkhani imeneyi ndipo anathandizidwa kumvetsa zinthu zimene anaonazo.

2 Masiku amenewo, ineyo Danieli, ndinakhala ndikulira+ kwa milungu itatu yathunthu. 3 Sindinadye chakudya chokoma, sindinadye nyama kapena kumwa vinyo ndipo sindinadzole mafuta aliwonse kwa milungu itatu yathunthu. 4 Pa tsiku la 24 la mwezi woyamba, ndili mʼmbali mwa mtsinje waukulu, mtsinje wa Tigirisi,*+ 5 ndinaona munthu atavala nsalu+ ndipo mʼchiuno mwake anali atamangamo lamba wa golide wa ku Ufazi. 6 Thupi lake linkanyezimira ngati mwala wa kulusolito,+ nkhope yake inkawala ngati mphezi, maso ake ankaoneka ngati miyuni yamoto, manja ake komanso mapazi ake ankaoneka ngati kopa*+ wonyezimira, ndipo mawu ake ankamveka ngati mawu a gulu lalikulu la anthu. 7 Ine ndekha Danieli, ndi amene ndinaona masomphenyawo+ koma amuna amene ndinali nawo sanawaone. Komabe iwo anayamba kunjenjemera kwambiri ndipo anathawa nʼkukabisala.

8 Choncho ndinatsala ndekha ndipo nditaona masomphenya odabwitsawa, mphamvu zonse zinandithera. Nkhope yanga imene inkaoneka yolemekezeka inasintha kwambiri, moti ndinalibenso mphamvu.+ 9 Kenako ndinamva munthu uja akulankhula. Koma nditamva kuti akulankhula, ndinagona pansi chafufumimba nʼkugona tulo tofa nato.+ 10 Ndiyeno ndinamva dzanja likundikhudza+ ndipo linandigwedeza kuti ndidzuke. Nditadzuka ndinagwada nʼkugwira pansi ndi manja anga. 11 Kenako iye anandiuza kuti:

“Iwe Danieli, munthu wokondedwa* kwambiri,+ mvetsera mwatcheru mawu amene ndikufuna kukuuza. Tsopano imirira chifukwa ine ndatumidwa kwa iwe.”

Atandiuza zimenezi, ndinaimirira koma ndikunjenjemera.

12 Ndiyeno munthu uja anandiuza kuti: “Iwe Danieli, usachite mantha.+ Mawu ako akhala akumveka kuyambira tsiku loyamba pamene unatsegula mtima wako kuti umvetse tanthauzo la zinthu zimenezi, ndiponso pamene unadzichepetsa pamaso pa Mulungu wako, ndipo ine ndabwera chifukwa cha mawu akowo.+ 13 Koma kalonga+ wa ufumu wa Perisiya ananditsekereza kwa masiku 21. Ndiyeno Mikayeli,*+ mmodzi wa akalonga aakulu,* anabwera kudzandithandiza. Pa nthawi imeneyo ndinakhalabe pomwepo pafupi ndi mafumu a Perisiya. 14 Ine ndabwera kudzakuthandiza kuti umvetse zimene zidzachitikire anthu a mtundu wako mʼmasiku otsiriza,+ chifukwa masomphenyawa ndi okhudza zimene zidzachitike mʼtsogolo.”+

15 Atandiuza mawu amenewa, ndinayangʼana pansi ndipo sindinathenso kulankhula. 16 Ndiyeno winawake wooneka ngati munthu anandiyandikira nʼkukhudza milomo yanga.+ Atatero, ndinayamba kulankhula ndipo ndinauza amene anali ataimirira patsogolo panga uja kuti: “Mbuyanga, ine ndikunjenjemera chifukwa cha zimene ndaona mʼmasomphenyawa ndipo mphamvu zandithera.+ 17 Choncho ine mtumiki wanu ndingathe bwanji kulankhula nanu mbuyanga?+ Panopa ndilibe mphamvu ndipo ndikupuma movutikira.”+

18 Ndiyeno wooneka ngati munthu uja anandikhudzanso nʼkundipatsa mphamvu.+ 19 Kenako anandiuza kuti: “Iwe munthu wokondedwa kwambiri,*+ usachite mantha.+ Mtendere ukhale nawe.+ Limba mtima, ndithu limba mtima.” Akulankhula nane, ndinalimbikitsidwa ndipo ndinanena kuti: “Lankhulani mbuyanga chifukwa inu mwandilimbikitsa.”

20 Ndiyeno anandiuza kuti: “Kodi ukudziwa chifukwa chake ndabwera kwa iwe? Tsopano ndibwerera kuti ndikamenyane ndi kalonga wa Perisiya.+ Ndikachoka, kalonga wa Girisi abwera. 21 Komabe ndikuuza zinthu zimene zinalembedwa mʼbuku la choonadi. Palibe aliyense amene akundithandiza kwambiri pa zinthu zimenezi kupatulapo Mikayeli,+ amene ndi kalonga wanu.”+

11 “Mʼchaka choyamba cha Dariyo+ Mmedi, ine ndinkamulimbikitsa ndipo ndinali ngati mpanda wolimba kwambiri kwa iye. 2 Zimene ndikufotokozere panopa ndi zoona:

Mu ufumu wa Perisiya mudzakhala mafumu atatu amene adzalamulire, ndipo mfumu ya nambala 4 idzasonkhanitsa chuma chambiri kuposa ena onsewa. Ndipo ikadzangokhala yamphamvu chifukwa cha chuma chakecho, idzagwiritsa ntchito chilichonse pomenyana ndi ufumu wa Girisi.+

3 Ndiyeno mfumu yamphamvu idzayamba kulamulira ndi mphamvu zazikulu+ ndipo idzachita zofuna zake. 4 Koma mfumuyo ikadzayamba kulamulira, ufumu wake udzasweka ndipo udzagawanika nʼkutengedwa ndi mphepo 4 zakumwamba,+ koma sudzapita kwa mbadwa zake ndipo maufumuwo sadzafanana ndi ufumu wake. Zimenezi zidzachitika chifukwa ufumu wake udzazulidwa nʼkuperekedwa kwa ena.

5 Mfumu yakumʼmwera, imene ndi mmodzi mwa akalonga ake, idzakhala yamphamvu. Koma iye* adzaigonjetsa ndipo adzalamulira ndi mphamvu zazikulu kuposa za iyeyo.*

6 Pakadzatha zaka zingapo iwo adzapanga mgwirizano ndipo mwana wamkazi wa mfumu yakumʼmwera adzapita kwa mfumu yakumpoto kuti apange mgwirizano. Koma mwana wamkaziyo sadzakhalanso ndi mphamvu ndipo mphamvu za mfumuyo zidzathanso. Mwana wamkaziyo adzaperekedwa mʼmanja mwa anthu ena pamodzi ndi amene anamubweretsa, amene anamubereka ndiponso amene ankamuchititsa kukhala wamphamvu masiku amenewo. 7 Kenako munthu wina wochokera ku mphukira ya mizu ya mwana wamkaziyo adzayamba kulamulira mʼmalo mwake* ndipo adzafika kwa gulu lankhondo nʼkupita kukaukira mzinda wokhala ndi mpanda wolimba kwambiri wa mfumu yakumpoto, moti munthuyo adzachita nayo nkhondo nʼkupambana. 8 Iye adzapita ku Iguputo ndi milungu yawo, zifaniziro zawo zachitsulo,* zinthu zawo zamtengo wapatali zasiliva ndi zagolide, pamodzi ndi anthu amene adzawagwire. Kwa zaka zingapo iye sadzalimbana ndi mfumu yakumpoto 9 imene idzapite kukaukira ufumu wa mfumu yakumʼmwera, kenako idzabwerera kudziko lakwawo.

10 Ana ake adzakonzekera nkhondo ndipo adzasonkhanitsa gulu lalikulu la asilikali. Iye adzafika mwamphamvu kwambiri nʼkudutsa mwachangu mʼdzikolo ngati madzi osefukira. Koma adzabwerera, ndipo adzachita nkhondo mpaka kumzinda wake wokhala ndi mpanda wolimba kwambiri.

11 Ndiyeno mfumu yakumʼmwera idzakwiya kwambiri ndipo idzapita kukamenyana ndi mfumu yakumpoto. Iye* adzakhala ndi gulu lalikulu, koma gululo lidzaperekedwa mʼmanja mwa mfumu inayo. 12 Gululo lidzatengedwa ndipo iye* adzadzitukumula mumtima mwake moti adzachititsa kuti anthu masauzandemasauzande aphedwe. Iye adzakhala wamphamvu, koma sadzagwiritsa ntchito bwino mphamvu zakezo kuti zimuthandize.

13 Kenako mfumu yakumpoto idzabwerera kwawo nʼkusonkhanitsa gulu lalikulu kwambiri kuposa loyamba lija. Ndiyeno patapita nthawi yaitali, pambuyo pa zaka zingapo, mfumuyo idzabwera ndi gulu lalikulu la asilikali lokhala ndi zida zambiri. 14 Mʼmasiku amenewo anthu ambiri adzaukira mfumu yakumʼmwera.

Ndiyeno anthu achiwawa* pakati pa anthu a mtundu wako adzatengeka ndi zochitika zimenezi ndipo adzayesa kukwaniritsa masomphenya, koma adzapunthwa.

15 Kenako mfumu yakumpoto idzabwera ndipo idzamanga malo okwera omenyerapo nkhondo nʼkulanda mzinda wokhala ndi mpanda wolimba kwambiri. Zida zankhondo zakumʼmwera* komanso asilikali ake osankhidwa mwapadera sadzatha kulimbana ndi mfumuyo. Iwo sadzakhala ndi mphamvu zoti alimbane nayo. 16 Mfumu imene idzabwere kudzamenyana nayo* idzachita zofuna zake ndipo palibe amene adzaime pamaso pake. Mfumuyo idzaimirira mʼDziko Lokongola+ ndipo idzakhala ndi mphamvu zoti nʼkupha anthu ambiri. 17 Mfumuyo idzatsimikiza mtima kuti ifike ndi gulu lonse la asilikali a ufumu wake ndipo adzachita nayo mgwirizano moti idzakwaniritsa zolinga zake. Iyo idzaloledwa kuti iwononge mwana wamkazi. Mwana wamkaziyo zinthu sizidzamuyendera bwino ndipo sadzapitiriza kukhala wokhulupirika kwa mfumuyo. 18 Idzatembenukira kumadera amʼmbali mwa nyanja ndipo idzalanda madera ambiri. Koma mtsogoleri wa asilikali adzathetsa khalidwe lake lonyoza, moti iye sadzanyozedwanso. Mtsogoleriyu adzachititsa kuti kunyozako kubwerere kwa mfumuyo. 19 Kenako idzabwerera* kumizinda yakwawo yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri. Kumeneko idzapunthwa nʼkugwa ndipo sidzakhalakonso.

20 Udindo wake udzatengedwa ndi wina amene adzachititse kuti wokhometsa msonkho* aziyendayenda mu ufumu waulemerero, koma mʼmasiku ochepa iye adzafa, osati chifukwa cha chiwawa kapena nkhondo.

21 Ndiyeno udindo wake udzatengedwa ndi munthu wonyozeka ndipo sadzamupatsa ulemerero waufumu. Iye adzabwera pa nthawi yamtendere* ndipo adzatenga ufumuwo mwachinyengo. 22 Iye adzagonjetsa magulu a asilikali okhala ngati madzi osefukira ndipo adzawonongedwa. Mtsogoleri+ wa pangano nayenso adzawonongedwa.+ 23 Ndipo chifukwa cha mgwirizano umene adzapange naye, iye adzachita zinthu mwachinyengo nʼkukhala ndi mphamvu pogwiritsa ntchito mtundu waungʼono. 24 Pa nthawi yamtendere,* iye adzalowa mʼmadera abwino kwambiri achigawocho ndipo adzachita zinthu zimene ngakhale makolo ake ndi makolo a makolo ake sanachitepo. Adzagawira anthu zinthu zimene zawonongedwa, zimene zalandidwa komanso katundu wosiyanasiyana. Adzakonzera ziwembu malo okhala ndi mipanda yolimba kwambiri, koma kwa kanthawi kochepa.

25 Iye adzasonkhanitsa mphamvu zake ndi kulimbitsa mtima wake kuti aukire mfumu yakumʼmwera ali ndi gulu lalikulu la asilikali. Mfumu yakumʼmwera nayonso idzakonzekera nkhondo ndipo idzasonkhanitsa gulu la asilikali lalikulu kwambiri komanso lamphamvu. Koma iye* sadzapambana chifukwa adzamukonzera chiwembu. 26 Anthu amene amadya zakudya zake zokoma ndi amene adzachititse kuti iye agonjetsedwe.

Gulu lake la asilikali lidzagonjetsedwa* ndipo anthu ambiri adzaphedwa.

27 Mafumu awiri amenewa adzakhala ndi mtima wofuna kuchita zoipa ndipo adzakhala patebulo limodzi nʼkumauzana zabodza. Koma zolinga zawo zonse sizidzatheka chifukwa mapeto adzafika pa nthawi yake.+

28 Choncho iye* adzabwerera kudziko lakwawo ali ndi katundu wochuluka ndipo adzakhala ndi mtima wofunitsitsa kuukira pangano lopatulika. Iye adzakwaniritsa zolinga zake nʼkubwerera kwawo.

29 Pa nthawi imene inaikidwiratu iye adzabweranso ndipo adzaukira mfumu yakumʼmwera. Koma sizidzakhala ngati mmene zinalili poyamba, 30 chifukwa sitima zapamadzi za ku Kitimu+ zidzabwera kudzamuukira ndipo adzachititsidwa manyazi.

Iye adzabwerera kwawo ndipo adzalankhula mawu amphamvu odzudzula* pangano lopatulika+ moti adzakwaniritsa zolinga zake. Adzabwerera kwawo ndithu ndipo adzayamba kuganizira za anthu amene akusiya pangano lopatulika. 31 Ndiyeno magulu a asilikali ake* adzachitapo kanthu* ndipo adzaipitsa malo opatulika,+ malo okhala ndi mpanda wolimba kwambiri komanso adzachotsa nsembe zoyenera kuperekedwa nthawi zonse.+

Iwo adzaika pamalowo chinthu chonyansa chobweretsa chiwonongeko.+

32 Anthu amene amachita zinthu zoipa zotsutsana ndi pangano adzawachititsa kuti ayambe mpatuko pogwiritsa ntchito mawu achinyengo. Koma anthu amene amadziwa Mulungu wawo adzapambana ndipo adzakwaniritsa zolinga zawo. 33 Anthu ozindikira+ pakati pa anthuwo adzathandiza anthu ambiri kuti amvetse zinthu. Kwa masiku angapo iwo adzapunthwa chifukwa cha lupanga, malawi a moto, kutengedwa ukapolo komanso chifukwa cha kuwonongedwa kwa zinthu zawo. 34 Koma akadzapunthwa adzapatsidwa thandizo lochepa, ndipo anthu ambiri adzakhala kumbali yawo pogwiritsira ntchito mawu achinyengo. 35 Ena mwa anthu ozindikirawo adzapunthwa. Zidzakhala choncho kuti ntchito yoyenga ichitike chifukwa cha iwowo ndiponso kuti anthu ozindikira atsukidwe ndi kuyeretsedwa+ mpaka nthawi ya mapeto, chifukwa mapetowo adzafika pa nthawi yake.

36 Mfumuyo idzachita zofuna zake ndipo idzadzikweza ndi kudzikuza kuposa mulungu aliyense. Iyo idzalankhula zinthu zodabwitsa zotsutsana ndi Mulungu wa milungu.+ Mfumuyo idzapambana mpaka nthawi ya mkwiyo itatha, chifukwa zimene Mulungu wakonza ziyenera kuchitika. 37 Mfumu imeneyi sidzalemekeza Mulungu wa makolo ake. Sidzaganiziranso zofuna za akazi kapena za mulungu wina aliyense koma idzadzikweza pamwamba pa aliyense. 38 Idzapereka ulemu kwa mulungu amene amalemekezedwa mʼmalo okhala ndi mipanda yolimba kwambiri. Idzapereka ulemu kwa mulungu amene makolo ake sanamudziwe. Idzachita zimenezi popereka kwa mulunguyo golide, siliva, miyala yamtengo wapatali ndi zinthu zamtengo wapatali. 39 Mfumuyo idzakwaniritsa zolinga zake polimbana ndi malo otetezeka kwambiri okhala ndi mipanda yolimba kwambiri ndipo idzachita zimenezi pamodzi ndi* mulungu wachilendo. Onse amene ali kumbali yake idzawapatsa* ulemerero waukulu ndipo idzachititsa kuti anthu oterowo alamulire pakati pa anthu ambiri. Idzagawa malo kwa munthu aliyense amene adzalipire.

40 Mu nthawi yamapeto mfumu yakumʼmwera idzayamba kukankhana* ndi mfumu yakumpoto ndipo mfumu yakumpotoyo idzabwera mwamphamvu kudzamenyana nayo. Idzabwera ndi magaleta, asilikali okwera pamahatchi ndi sitima zambiri zapamadzi ndipo idzalowa mʼmayiko nʼkudutsamo mofulumira ngati madzi osefukira. 41 Idzalowanso mʼDziko Lokongola+ ndipo idzachititsa kuti mayiko ambiri apunthwe. Koma Edomu, Mowabu ndi mbali yaikulu ya Aamoni adzapulumuka mʼmanja mwake. 42 Mfumuyo idzapitiriza kutambasula dzanja lake kuti izilamulira mayiko ndipo dziko la Iguputo silidzapulumuka. 43 Idzalamulira chuma chobisika cha golide ndi siliva komanso zinthu zonse zamtengo wapatali za Iguputo. Anthu a ku Libiya ndi a ku Itiyopiya adzamutsatira.

44 Koma malipoti ochokera kumʼmawa* ndi kumpoto adzaisokoneza ndipo idzapita ndi mkwiyo waukulu kukafafaniza ndi kuwononga ambiri. 45 Ndipo mfumuyo idzamanga matenti achifumu pakati pa nyanja yaikulu ndi phiri lopatulika la Dziko Lokongola.+ Ndiyeno pamapeto pake mfumuyo idzawonongedwa ndipo sipadzapezeka woithandiza.”

12 “Pa nthawi imeneyo Mikayeli,*+ kalonga wamkulu+ amene waimirira kuti athandize anthu a mtundu wako,* adzaimirira. Ndiyeno padzafika nthawi yamasautso imene sinakhalepo kuyambira pamene mtundu woyambirira wa anthu unakhalapo kudzafika nthawi imeneyo. Pa nthawi imeneyo anthu a mtundu wako, aliyense amene dzina lake lidzakhala litalembedwa mʼbuku, adzapulumuka.+ 2 Anthu ambiri amene agona munthaka adzadzuka. Ena adzalandira moyo wosatha koma ena adzachititsidwa manyazi komanso adzadedwa mpaka kalekale.

3 Anthu ozindikira adzawala kwambiri ngati kuwala kwa kuthambo. Ndipo amene akuthandiza anthu ambiri kuti akhale olungama adzawala ngati nyenyezi mpaka muyaya.

4 Koma iwe Danieli, sunga mawuwa mwachinsinsi ndipo umate bukuli mpaka nthawi yamapeto.+ Anthu ambiri adzaphunzira bukuli mokwanira* ndipo adzadziwa zinthu zambiri zoona.”+

5 Ndiyeno ineyo Danieli nditayangʼana, ndinaona angelo ena awiri ataimirira. Mngelo mmodzi anaima mʼmbali mwa mtsinje tsidya lino ndipo wina anaima tsidya linalo.+ 6 Kenako mmodzi mwa angelowo anafunsa munthu amene anavala nsalu uja,+ amene anaimirira pamwamba pa madzi amumtsinjewo, kuti: “Kodi padzatenga nthawi yaitali bwanji kuti zinthu zodabwitsazi zikwaniritsidwe zonse?” 7 Kenako ndinamva munthu amene anavala nsalu uja, amene anali pamwamba pa madzi amumtsinje akuyankha. Iye anakweza mʼmwamba dzanja lake lamanja ndi lamanzere nʼkulumbira pa Mulungu amene adzakhala ndi moyo mpaka kalekale,+ ndipo anati: “Padzadutsa nthawi imodzi yoikidwiratu, nthawi ziwiri zoikidwiratu ndi hafu ya nthawi yoikidwiratu.* Ndipo akadzangomaliza kuphwanyaphwanya mphamvu za anthu oyera,+ zinthu zonsezi zidzafika pamapeto.”

8 Tsopano ine ndinamva zimene ananenazo, koma sindinadziwe tanthauzo lake.+ Choncho ndinafunsa kuti: “Inu mbuyanga, kodi zinthu zimenezi zidzatha bwanji?”

9 Iye anandiyankha kuti: “Pita Danieli, chifukwa mawuwa akuyenera kusungidwa mwachinsinsi ndi kumatidwa mpaka nthawi yamapeto.+ 10 Anthu ambiri adzadzitsuka, adzadziyeretsa ndipo adzayengedwa.+ Anthu oipa adzachita zinthu zoipa ndipo palibe munthu woipa aliyense amene adzamvetsetse mawu amenewa, koma anthu ozindikira adzawamvetsetsa.+

11 Kuchokera pa nthawi imene nsembe zoyenera kuperekedwa nthawi zonse+ zidzachotsedwe, ndiponso pamene chinthu chonyansa chobweretsa chiwonongeko chidzaikidwe,+ padzadutsa masiku 1,290.

12 Wosangalala ndi munthu amene akuyembekezera* mpaka kufika kumapeto kwa masiku 1,335.

13 Koma iwe Danieli upirire mpaka mapeto ndipo udzapuma. Ndiyeno pamapeto amasikuwo udzauka kuti ulandire gawo lako.”+

Kapena kuti, “mʼkachisi wa.”

Kumene ndi ku Babeloniya.

Kapena kuti, “kukachisi.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “ana a Isiraeli.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “ana.”

Mabaibulo ena amati, “kuwadyetsa.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “ana aamuna a Yuda.”

Kutanthauza, “Woweruza Wanga ndi Mulungu.”

Kutanthauza, “Yehova Wasonyeza Kukoma Mtima.”

Nʼkutheka kuti likutanthauza kuti, “Ndi Ndani Amene Angafanane ndi Mulungu?”

Kutanthauza, “Yehova Wathandiza.”

Amenewa ndi mayina a ku Babulo.

Kapena kuti, “Sadirake.”

Kapena kuti, “Mesake.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “ana.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “kuti mutu wanga ukhale.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “ana.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “onenepa.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “ana.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “ana.”

Kameneka kanali kagulu ka anthu amene anali ndi luso lolosera zamʼtsogolo komanso kuphunzira zokhudza nyenyezi.

Mawu a pa Da 2:4b mpaka 7:28 poyambirira analembedwa mʼChiaramu.

Mabaibulo ena amati, “kudzala; milu ya ndowe.”

Kapena kuti, “kuyambira kalekale mpaka kalekale.”

Kapena kuti, “zamkuwa.”

“Mankhusu” ndi makoko amene amachotsa ku mbewu ngati mpunga popuntha ndipo amatha kuwauluza ndi mphepo.

Kapena kuti, “ana a anthu,” amene ndi anthu wamba.

Kapena kuti, “Sadirake.”

Kapena kuti, “Mesake.”

Pafupifupi mamita 27. Onani Zakumapeto B14.

Pafupifupi mamita 2.7. Onani Zakumapeto B14.

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Kapena kuti, “kukanenera zoipa.”

Kapena kuti, “Sadirake.”

Kapena kuti, “Mesake.”

Kapena kuti, “ndipo anawakwiyira kwambiri.”

Kapena kuti, “anaona kuti motowo unalibe mphamvu pa iwo.”

Kapena kuti, “kupereka matupi awo.”

Mabaibulo ena amati, “kudzala; milu yandowe.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “inachititsa kuti zinthu zizimuyendera bwino.”

Kameneka kanali kagulu ka anthu amene anali ndi luso lolosera zamʼtsogolo komanso kuphunzira zokhudza nyenyezi.

Kapena kuti, “wamkuwa.”

Kapena kuti, “wamkuwa.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Kapena kuti, “yamkuwa.”

Kameneka kanali kagulu ka anthu amene anali ndi luso lolosera zamʼtsogolo komanso kuphunzira zokhudza nyenyezi.

Kameneka kanali kagulu ka anthu amene anali ndi luso lolosera zamʼtsogolo komanso kuphunzira zokhudza nyenyezi.

Mʼchilankhulo choyambirira, “komanso kumasula mfundo.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “komanso kumasula mfundo.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Mʼchilankhulo choyambirira, “pakamwa pa.”

Mabaibulo ena amati, “sanamubweretsere oimba.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “komanso tulo tinamuthawa.”

Kapena kuti, “onyada.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Masauzande 1,000.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “10 sauzande kuchulukitsa ndi 10 sauzande.”

Kapena kuti, “onyada.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “amene adzauke padziko lapansi.”

Kapena kuti, “zamkuwa.”

Kapena kuti, “onyada.”

Kutanthauza nthawi zitatu ndi hafu.

Kapena kuti, “yokhala ndi mpanda wolimba kwambiri.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼmanja mwake.”

Kapena kuti, “kolowera dzuwa.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼdzanja la.”

Kapena kuti, “kotulukira dzuwa.”

Mabaibulo ena amati, “Popanda chenjezo.”

Amenewa ndi mabuku opatulika.

Mʼchilankhulo choyambirira, “nkhope yamanyazi.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “nkhope yamanyazi.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “oweruza athu amene ankatiweruza.”

Kapena kuti, “Koma sitinakhazike pansi mtima wa Yehova Mulungu wathu.”

Kapena kuti, “kukhulupirika kwanu.”

Kapena kuti, “wamtengo wapatali kwambiri.”

Imeneyi ndi milungu ya zaka ndipo ikukwana zaka 490.

Mʼchilankhulo choyambirira, “mneneri.”

Kapena kuti, “Malo Oyera Koposa.”

Kapena kuti, “Wodzozedwa.”

Zikuoneka kuti apa akunena Mesiya.

Mʼchilankhulo choyambirira, “Hidekeli.”

Kapena kuti, “mkuwa.”

Kapena kuti, “wamtengo wapatali.”

Kutanthauza, “Ndi Ndani Angafanane ndi Mulungu?”

Kapena kuti, “kalonga wolemekezeka kwambiri.”

Kapena kuti, “wamtengo wapatali kwambiri.”

Apa zikuoneka kuti akunena mfumu yakumpoto.

Apa zikuoneka kuti akunena mfumu yakumʼmwera.

Apa zikuoneka kuti akunena mfumu yakumʼmwera.

Kapena kuti, “zachitsulo chosungunula.”

Apa zikuoneka kuti akunena mfumu ya kumpoto.

Apa zikuoneka kuti akunena mfumu yakumʼmwera.

Kapena kuti, “ana a anthu achifwamba.”

Kapena kuti, “Magulu a asilikali akumʼmwera.”

Apa zikuoneka kuti akunena mfumu yakumʼmwera.

Apa zikuoneka kuti akunena mfumu yakumpoto.

Mawu amene amasuliridwa kuti “wokhometsa msonkho” akhozanso kutanthauza munthu amene amalemba anthu ntchito yausilikali.

Mabaibulo ena amati, “popanda chenjezo.”

Mabaibulo ena amati, “Popanda chenjezo.”

Apa zikuoneka kuti akunena mfumu yakumpoto.

Kapena kuti, “lidzakokololedwa ndi madzi osefukira.”

Apa zikuoneka kuti akunena mfumu yakumpoto.

Kapena kuti, “ndipo adzaonetsa mkwiyo wake wonse.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “manja ake.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “adzaimirira.”

Kapena kuti, “mothandizidwa ndi.”

Mabaibulo ena amati, “Aliyense amene iye akumuvomereza adzamupatsa.”

Kapena kuti, “kugundana.”

Kapena kuti, “kotulukira dzuwa.”

Kutanthauza, “Ndi Ndani Angafanane ndi Mulungu.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “ana aamuna a anthu ako.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “adzayenda uku ndi uku.”

Zimenezi ndi nthawi zitatu ndi hafu.

Kapena kuti, “amene akudikira mwachidwi.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena