KALATA YOYAMBA YOPITA KWA ATESALONIKA
1 Ine Paulo ndili limodzi ndi Silivano*+ komanso Timoteyo+ ndipo ndikulembera mpingo wa Atesalonika, womwe ndi wogwirizana ndi Mulungu Atate komanso Ambuye Yesu Khristu kuti:
Kukoma mtima kwakukulu ndi mtendere zikhale nanu.
2 Nthawi zonse timathokoza Mulungu tikamakutchulani nonsenu mʼmapemphero athu.+ 3 Timachita zimenezi chifukwa nthawi zonse timakumbukira ntchito zanu zachikhulupiriro, ntchito zanu zachikondi komanso kupirira kwanu chifukwa cha chiyembekezo chimene muli nacho+ mwa Ambuye wathu Yesu Khristu, pamaso pa Mulungu amene ndi Atate wathu. 4 Chifukwa tikudziwa, inu abale okondedwa ndi Mulungu, kuti iye ndi amene anakusankhani. 5 Tikutero chifukwa pamene tinkalalikira uthenga wabwino kwa inu, sitinkangolankhula basi, koma uthengawo unali wamphamvu, unabwera ndi mzimu woyera komanso tinalalikira motsimikiza mtima kwambiri. Inunso mukudziwa zimene tinakuchitirani pofuna kukuthandizani. 6 Munalandira mawuwo ndi chimwemwe chimene mzimu woyera+ umapereka ngakhale kuti munali pamavuto aakulu. Pamenepa munatsanzira ifeyo+ komanso munatsanzira Ambuye,+ 7 moti munakhala chitsanzo kwa okhulupirira onse ku Makedoniya ndi ku Akaya.
8 Sikuti mawu a Yehova* ochokera kwa inu amveka ku Makedoniya ndi ku Akaya kokha, koma kwina kulikonse chikhulupiriro chanu mwa Mulungu chafalikira,+ moti ife sitikufunika kunenapo kanthu. 9 Chifukwa iwo akunenabe za mmene ife tinakumanirana ndi inu koyamba komanso mmene inu munasiyira mafano anu nʼkutembenukira kwa Mulungu,+ kuti muzitumikira Mulungu wamoyo ndi woona. 10 Munatembenukiranso kwa Mulungu kuti muziyembekezera Mwana wake kuchokera kumwamba,+ amene anamuukitsa kwa akufa. Mwanayo ndi Yesu, amene akutipulumutsa ku mkwiyo umene ukubwerawo.+
2 Kunena zoona, inuyo mukudziwa abale, kuti ulendo wathu wobwera kwa inu sunali wopanda phindu.+ 2 Chifukwa ngakhale kuti poyamba tinavutika komanso kuchitiridwa zachipongwe ku Filipi,+ monga mmene mukudziwira, tinalimba mtima mothandizidwa ndi Mulungu wathu kuti tikuuzeni uthenga wabwino wa Mulungu+ pa nthawi imene anthu ankatitsutsa kwambiri.* 3 Zimene tikukulimbikitsani kuti muchite sizikuchokera mʼmaganizo olakwika kapena odetsedwa ndipo sitikuzinena mwachinyengo. 4 Koma Mulungu wavomereza kuti tipatsidwe ntchito yolalikira uthenga wabwino. Choncho sitikulankhula nʼcholinga chosangalatsa anthu, koma Mulungu amene amafufuza mitima yathu.+
5 Ndipotu mukudziwa kuti sitinayambe talankhulapo mawu okuyamikirani mwachinyengo, kapena kuchita zachiphamaso ndi zolinga zadyera.+ Mulungu ndi mboni yathu. 6 Komanso sitinkafuna ulemerero wochokera kwa anthu, kaya kuchokera kwa inu kapena kwa anthu ena, ngakhale kuti monga atumwi a Khristu+ tikanatha kupempha kuti mutilipirire zinthu zina kuti mutithandize. 7 Mʼmalomwake, tinakusonyezani chikondi komanso kukoma mtima ngati mmene mayi woyamwitsa amachitira posamalira ana ake mwachikondi. 8 Choncho popeza timakukondani kwambiri,+ tinkafunitsitsa* kukuuzani uthenga wabwino wa Mulungu komanso kupereka miyoyo yathu yeniyeniyo+ kuti tikuthandizeni.
9 Ndithudi abale, mukukumbukira kuti tinayesetsa kugwira ntchito mwakhama ndi mphamvu zathu zonse. Tinkagwira ntchito usiku ndi masana kuti aliyense wa inu asatilipirire kanthu kalikonse pofuna kutithandiza,+ pamene tinkalalikira uthenga wabwino wa Mulungu kwa inu. 10 Pamene tinali ndi inu okhulupirira, tinali okhulupirika, tinkachita zinthu zachilungamo ndiponso tinalibe chifukwa chotinenezera. Inuyo komanso Mulungu ndinu mboni zathu. 11 Inu mukudziwa bwino kuti aliyense wa inu tinkamudandaulira, kumulimbikitsa komanso kumulangiza+ ngati mmene bambo+ amachitira ndi ana ake. 12 Tinkachita zimenezi nʼcholinga choti mupitirize kuyenda mʼnjira imene Mulungu amafuna.+ Iye ndi amene akukuitanani kuti mulowe mu Ufumu wake+ ndi kulandira ulemerero.+
13 Ndithudi, nʼchifukwa chake ifenso timathokoza Mulungu mosalekeza,+ chifukwa pamene munalandira mawu a Mulungu amene munamva kwa ife, simunawalandire monga mawu a anthu, koma mmene alilidi, monga mawu a Mulungu. Mawu amenewa akugwiranso ntchito mwa inu okhulupirira. 14 Chifukwa inu abale munatsanzira mipingo ya Mulungu yogwirizana ndi Khristu Yesu imene ili ku Yudeya. Tikutero chifukwa munayamba kuvutitsidwa ndi anthu akwanu,+ ngati mmene iwowonso akuvutitsidwira ndi Ayuda. 15 Iwo anafika popha Ambuye Yesu+ komanso aneneri ndipo ife anatizunza.+ Kuwonjezera pamenepo, iwo sakusangalatsa Mulungu, koma akuchita zinthu zimene sizingapindulitse anthu onse. 16 Iwo akuchita zimenezi pamene akuyesa kutiletsa kulalikira kwa anthu a mitundu ina zimene angachite kuti adzapulumuke.+ Pochita zimenezi, nthawi zonse akuwonjezera machimo awo. Koma tsopano mkwiyo wake wawafikira.+
17 Koma pamene tinakakamizika kusiyana ndi inu abale, kwa nthawi yochepa (pamasomʼpamaso osati mumtima mwathu), tinayesetsa kwambiri kuti tikuoneni pamasomʼpamaso* chifukwa ndi zimene tinkalakalaka kwambiri. 18 Choncho tinkafuna kubwera kwa inu ndipo ineyo Paulo ndinayesa kuti ndibwere, osati kamodzi kokha koma kawiri, koma Satana anatchinga njira yathu. 19 Kodi chiyembekezo chathu kapena chimwemwe chathu nʼchiyani? Kodi mphoto* imene tidzainyadire pamaso pa Ambuye wathu Yesu, pa nthawi ya kukhalapo kwake nʼchiyani? Kodi si inuyo?+ 20 Ndithudi, inu ndinu ulemerero wathu komanso chimwemwe chathu.
3 Choncho pamene sitinathenso kupirira, tinaona kuti ndi bwino kuti tipitirize kukhala ku Atene.+ 2 Ndiye tinatumiza Timoteyo+ mʼbale wathu, yemwe ndi mtumiki wa Mulungu* amene akulengeza uthenga wabwino wonena za Khristu. Tinamutumiza kuti adzakulimbikitseni ndi kukutonthozani nʼcholinga choti chikhulupiriro chanu chikhale cholimba. 3 Tinachita zimenezi kuti pasapezeke aliyense amene chikhulupiriro chake chafooka* ndi masautso amenewa. Chifukwa inunso mukudziwa kuti sitingapewe kukumana ndi mavuto ngati amenewa.*+ 4 Chifukwa pamene tinali nanu limodzi, tinkakuuziranitu kuti tidzakumana ndi mavuto ndipo monga mmene mukudziwira, zimene tinkakuuzanizo ndi zimene zachitikadi.+ 5 Nʼchifukwa chake pamene sindinathenso kupirira, ndinatuma Timoteyo kwa inu kuti ndidziwe za kukhulupirika kwanu.+ Ndimadera nkhawa kuti mwina Woyesayo+ anakuyesani ndipo nʼkutheka kuti ntchito imene tinagwira mwakhama inangopita pachabe.
6 Koma Timoteyo wangofika kumene kuno kuchokera kumeneko+ ndipo watiuza nkhani yabwino yokhudza kukhulupirika kwanu ndi chikondi chanu. Watiuza kuti mukupitiriza kutikumbukira ndipo mumatikonda komanso kuti mukulakalaka kutiona ngati mmene ifenso tikulakalakira kukuonani. 7 Nʼchifukwa chake abale, mʼmavuto athu onse* komanso mʼmasautso athu onse tatonthozedwa chifukwa cha inu komanso chifukwa cha kukhulupirika kumene mukusonyeza.+ 8 Chifukwa ife timapeza mphamvu* inu mukakhala olimba mwa Ambuye. 9 Kodi Mulungu tingamuthokoze bwanji kuti timubwezere chifukwa cha chimwemwe chachikulu chimene tili nacho pamaso pa Mulungu wathu chifukwa cha inu? 10 Usiku ndi masana timapemphera mopembedzera kuchokera pansi pamtima kuti tidzakuoneni pamasomʼpamaso* nʼkukupatsani zimene zikufunika kuti chikhulupiriro chanu chikhale cholimba.+
11 Tsopano Mulungu amenenso ndi Atate wathu komanso Ambuye wathu Yesu, atithandize kuti zitheke kubwera kwa inu. 12 Komanso, Ambuye akuthandizeni kuti muzikondana kwambiri ndiponso kuti muzikonda anthu ena+ ngati mmene ife timakukonderani. 13 Achite zimenezi kuti alimbitse mitima yanu kuti mukhale opanda cholakwa ndi oyera pamaso pa Mulungu+ amene ndi Atate wathu, pa nthawi ya kukhalapo kwa Ambuye wathu Yesu,+ limodzi ndi oyera ake onse.
4 Pomalizira abale, tinakupatsani malangizo a mmene muyenera kuyendera kuti muzisangalatsa Mulungu+ ndipo mukuchitadi zimenezo. Ndiye tikukupemphani komanso kukuchondererani mʼdzina la Ambuye Yesu kuti mupitirize kuchita zimenezi kuposa mmene mukuchitira. 2 Chifukwa mukudziwa malangizo* amene tinakupatsani mʼdzina la Ambuye Yesu.
3 Mulungu akufuna kuti mukhale oyera+ komanso kuti muzipewa chiwerewere.*+ 4 Aliyense wa inu azidziwa kulamulira thupi lake+ kuti likhale loyera+ komanso lolemekezeka pamaso pa Mulungu. 5 Musakhale ngati anthu a mitundu ina omwe sadziwa Mulungu+ komanso ali ndi chilakolako chosalamulirika cha kugonana+ ndipo sakhutiritsidwa. 6 Pasapezeke aliyense wopweteka mʼbale wake pa nkhani imeneyi nʼkumubweretsera mavuto, chifukwa Yehova* adzapereka chilango kwa munthu aliyense amene akuchita zinthu zimenezi, monga mmene tinakuuzirani kale komanso kukuchenjezani mwamphamvu. 7 Chifukwa Mulungu sanatiitane kuti tizichita makhalidwe odetsa, koma kuti tikhale oyera.+ 8 Choncho munthu amene akunyalanyaza machenjezo amenewa sakunyalanyaza munthu, koma Mulungu+ amene amakupatsani mzimu wake woyera.+
9 Koma zokhudza kukonda abale,+ nʼzosafunika kuti tichite kukulemberani chifukwa inuyo, Mulungu amakuphunzitsani kuti muzikondana.+ 10 Ndipotu mukuchita kale zimenezi kwa abale onse ku Makedoniya konse. Koma tikukulimbikitsani abale kuti mupitirize kuchita zimenezi kuposa mmene mukuchitira. 11 Muziyesetsa kukhala mwamtendere,+ musamalowerere nkhani za ena+ ndipo muzigwira ntchito ndi manja anu+ mogwirizana ndi malangizo amene tinakupatsani. 12 Muzichita zimenezi kuti mukhale ndi makhalidwe amene angachititse kuti anthu akunja azikulemekezani+ ndiponso kuti mukhale osasowa kanthu.
13 Komanso abale, sitikufuna kuti mukhale osadziwa zokhudza amene akugona mu imfa,+ kuti musakhale ndi chisoni chofanana ndi cha anthu amene alibe chiyembekezo.+ 14 Chifukwa ngati timakhulupirira kuti Yesu anafa nʼkuukitsidwa,+ ndiye kuti Mulungu adzaukitsanso amene akugona mu imfa kudzera mwa Yesu,+ kuti akakhale naye* limodzi. 15 Zimene tikukuuzani mogwirizana ndi mawu a Yehova* nʼzakuti, ife amene tipitirize kukhala ndi moyo mpaka pa nthawi ya kukhalapo kwa Ambuye, sitidzakhala patsogolo pa amene akugona mu imfa. 16 Chifukwa Ambuyewo adzatsika kuchoka kumwamba ndi mfuu yolamula. Mawu awo adzamveka kuti ndi a mkulu wa angelo+ ndipo adzanyamula lipenga la Mulungu mʼdzanja lawo. Ndipo amene anafa mwa Khristu adzakhala oyambirira kuuka.+ 17 Pambuyo pake ife amene tidzakhale tidakali ndi moyo, limodzi ndi iwowo, tidzatengedwa kupita mʼmitambo+ kukakumana ndi Ambuye+ mumlengalenga ndipo tizikakhala ndi Ambuye nthawi zonse.+ 18 Choncho pitirizani kulimbikitsana ndi mawu amenewa.
5 Koma tsopano za nthawi ndi nyengo abale, simukufunika kuti tikulembereni chilichonse. 2 Chifukwa inuyo mukudziwa bwino kuti tsiku la Yehova*+ lidzabwera ndendende ngati wakuba usiku.+ 3 Akadzangonena kuti, “Bata ndi mtendere!” nthawi yomweyo adzawonongedwa. Tsoka limeneli lidzawagwera modzidzimutsa+ ngati ululu umene mkazi woyembekezera amamva akatsala pangʼono kubereka ndipo sadzapulumuka. 4 Koma inu abale simuli mumdima kuti tsiku limenelo lidzakudzidzimutseni ngati mmene akuba amadzidzimukira kunja kukawachera. 5 Chifukwa nonsenu ndi ana a kuwala ndiponso ana a masana.+ Si ife a usiku kapena a mdima.+
6 Choncho tisapitirize kugona ngati mmene ena onse akuchitira,+ koma tikhalebe maso+ ndipo tikhalebe oganiza bwino.+ 7 Chifukwa amene akugona amagona usiku ndipo amene amaledzera, amaledzera usiku.+ 8 Koma ife amene tili a masana, tikhalebe oganiza bwino ndipo tivale chodzitetezera pachifuwa cha chikhulupiriro ndi chikondi. Tivalenso chiyembekezo cha chipulumutso ngati chipewa,+ 9 chifukwa Mulungu sanatisankhe kuti adzatilange, koma anatisankha kuti tidzapulumuke+ chifukwa cha zimene Ambuye wathu Yesu Khristu anachita. 10 Iye anatifera,+ kuti kaya tikhala maso kapena tigona,* tikhale ndi moyo limodzi ndi iye.+ 11 Choncho pitirizani kutonthozana ndi kulimbikitsana+ ngati mmene mukuchitira.
12 Tsopano tikukupemphani abale, kuti muzilemekeza anthu amene akugwira ntchito mwakhama pakati panu, amenenso amakutsogolerani mwa Ambuye komanso kukulangizani. 13 Muziwasonyeza chikondi komanso ulemu waukulu chifukwa cha ntchito yawo.+ Muzikhala mwamtendere pakati panu.+ 14 Komanso tikukulimbikitsani abale, kuti muzichenjeza* anthu ochita zosalongosoka,+ muzilankhula molimbikitsa kwa anthu amene ali ndi nkhawa,* muzithandiza ofooka, muzikhala oleza mtima kwa onse.+ 15 Onetsetsani kuti pasapezeke wobwezera choipa pa choipa kwa wina aliyense,+ koma nthawi zonse muziyesetsa kuchita zabwino kwa okhulupirira anzanu ndi kwa ena onse.+
16 Muzikhala osangalala nthawi zonse.+ 17 Muzipemphera nthawi zonse.+ 18 Muzithokoza pa chilichonse.+ Mulungu akufuna kuti muzichita zimenezi chifukwa ndinu otsatira a Khristu Yesu. 19 Musazimitse moto wa mzimu.+ 20 Musamanyoze mawu aulosi.+ 21 Muzifufuza zinthu zonse nʼkutsimikizira zimene zili zabwino+ ndipo gwirani mwamphamvu zabwinozo. 22 Muzipewa zoipa zamtundu uliwonse.+
23 Mulungu wamtendereyo akupatuleni kuti muchite utumiki wake. Ndipo pa mbali zonse abale, mzimu wanu, moyo wanu komanso thupi lanu, zikhale zopanda chilema kapena cholakwa chilichonse, pa nthawi ya kukhalapo kwa Ambuye wathu Yesu Khristu.+ 24 Amene akukuitanani ndi wokhulupirika ndipo adzachitadi zimenezi.
25 Abale, pitirizani kutipempherera.+
26 Mupereke moni kwa abale onse ndipo mukisane ndi mtima woyera.
27 Ndikukupemphani mwa Ambuye kuti kalatayi iwerengedwe kwa abale onse.+
28 Kukoma mtima kwakukulu kwa Ambuye wathu Yesu Khristu kukhale nanu.
Amene ankadziwikanso kuti Sila.
Onani Zakumapeto A5.
Mabaibulo ena amati, “nthawi imene tinkavutika kwambiri.”
Kapena kuti, “tinali osangalala.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “tione nkhope zanu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “chisoti chachitsulo chooneka ngati nkhata.”
Mabaibulo ena amati, “yemwe ndi wantchito mnzake wa Mulungu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “amene wasochera.”
Kapena kuti, “mukudziwa kuti tikuyenera kukumana ndi zimenezi.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “pa zosowa zathu zonse.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “timakhala ndi moyo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “kuti tidzaone nkhope zanu.”
Kapena kuti, “malamulo.”
MʼChigiriki por·nei′a. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Onani Zakumapeto A5.
Kutanthauza Yesu.
Onani Zakumapeto A5.
Onani Zakumapeto A5.
Kapena kuti, “tigona mu imfa.”
Kapena kuti, “muzilangiza.”
Kapena kuti, “amene afooka.”