Ekisodo
40 Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti: 2 “Pa tsiku loyamba la mwezi woyamba, udzamange chihema kapena kuti chihema chokumanako.+ 3 Mkati mwake udzaikemo likasa la Umboni+ ndipo udzatchinge kumene kuli Likasalo ndi katani.+ 4 Mʼchihemacho udzaikemonso tebulo+ ndipo udzaikepo zinthu zake mwadongosolo. Kenako udzaikemo choikapo nyale+ nʼkuyatsa nyale zake.+ 5 Ndiyeno udzaike guwa lansembe zofukiza lagolide+ patsogolo pa likasa la Umboni, nʼkuika nsalu yotchinga pakhomo la chihema.+
6 Udzaike guwa lansembe zopsereza+ patsogolo pa khomo la chihema kapena kuti chihema chokumanako. 7 Ndipo udzaike beseni pakati pa chihema chokumanako ndi guwa lansembe nʼkuthiramo madzi.+ 8 Kenako udzatchinge bwalo la chihema+ ndi mpanda ndipo pakhomo pa bwalolo udzaikepo nsalu yake yotchinga.+ 9 Kenako udzatenge mafuta odzozera+ nʼkudzoza chihema ndi zonse zimene zili mkati mwake+ ndipo udzachiyeretse pamodzi ndi ziwiya zake zonse kuti chikhale chopatulika. 10 Udzadzozenso guwa lansembe zopsereza ndi ziwiya zake zonse nʼkuliyeretsa, kuti guwalo lidzakhale lopatulika kwambiri.+ 11 Ndiponso udzadzoze beseni ndi choikapo chake nʼkuliyeretsa.
12 Kenako udzabweretse Aroni ndi ana ake pafupi ndi khomo la chihema chokumanako ndipo udzawasambitse ndi madzi.+ 13 Ukatero udzaveke Aroni zovala zopatulika+ kenako nʼkumudzoza+ komanso kumuyeretsa ndipo adzatumikira monga wansembe wanga. 14 Kenako udzatenge ana ake nʼkuwaveka mikanjo.+ 15 Udzawadzoze ngati mmene unadzozera bambo awo+ kuti atumikire monga ansembe anga. Iwo akadzadzozedwa adzapitiriza kutumikira monga ansembe mʼmibadwo yawo yonse.”+
16 Mose anachita zonse mogwirizana ndi zimene Yehova anamulamula.+ Anachitadi zomwezo.
17 Choncho mʼmwezi woyamba wa chaka chachiwiri, pa tsiku loyamba la mweziwo, anamanga chihema.+ 18 Pamene Mose ankamanga chihemacho, anayala pansi zitsulo zake+ nʼkukhazikamo mafelemu.+ Ndiyeno analowetsa ndodo zake+ nʼkuimika zipilala pamalo ake. 19 Atatero anayala nsalu+ yophimba pachihemacho ndi inanso yophimba+ pamwamba pake, mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose.
20 Kenako anatenga Umboni+ ndi kuuika mu Likasa,+ ndipo analowetsa ndodo zonyamulira+ mʼmbali mwa Likasalo nʼkuika chivundikiro+ pamwamba pa Likasa.+ 21 Atatero analowetsa Likasa mʼchihema nʼkuika katani+ pamalo ake ndipo inatchinga likasa la Umboni,+ mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose.
22 Ndiyeno analowetsa tebulo+ mʼchihema chokumanako nʼkuliika kumbali yakumpoto ya chihemacho, kunja kwa katani. 23 Kenako anaika mkate+ pamalo ake pamaso pa Yehova, mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose.
24 Anaika choikapo nyale+ mʼchihema chokumanako patsogolo pa tebulo, kumbali yakumʼmwera ya chihemacho. 25 Ndipo anayatsa nyalezo+ pamaso pa Yehova, mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose.
26 Kenako anaika guwa lansembe lagolide+ mʼchihema chokumanako patsogolo pa katani, 27 kuti azifukizirapo zofukiza+ zonunkhira,+ mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose.
28 Atatero anaika nsalu yotchinga+ pakhomo la chihema.
29 Ndiyeno anaika guwa lansembe zopsereza+ pakhomo la chihema kapena kuti chihema chokumanako, kuti aziperekerapo nsembe yopsereza+ ndi nsembe yambewu, mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose.
30 Kenako anaika beseni pakati pa chihema chokumanako ndi guwa lansembe nʼkuthiramo madzi osamba.+ 31 Mose, Aroni ndi ana ake ankasamba mʼmanja ndi mapazi awo pamenepo. 32 Akamalowa mʼchihema chokumanako ndiponso akamapita kuguwa lansembe ankasamba,+ mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose.
33 Pomaliza anamanga mpanda kuzungulira bwalo+ la chihema ndi guwa lansembe ndipo anaika nsalu yotchinga pakhomo la bwalolo.+
Choncho Mose anamaliza ntchitoyo. 34 Kenako mtambo unayamba kuphimba chihema chokumanako ndipo ulemerero wa Yehova unadzaza mʼchihemacho.+ 35 Mose sanathenso kulowa mʼchihema chokumanako, chifukwa mtambo unali utaphimba chihemacho ndipo munadzaza ulemerero wa Yehova.+
36 Mʼzigawo zonse za ulendo wawo, mtambowo ukachoka pamwamba pa chihemacho nʼkukwera mʼmwamba, Aisiraeli ankanyamuka nʼkuyamba ulendo.+ 37 Koma ukapanda kukwera mʼmwamba, iwo sankanyamuka mpaka tsiku limene udzakwere.+ 38 Mtambo wa Yehova unkakhala pamwamba pa chihema masana ndipo usiku pankakhala moto. Nyumba yonse ya Isiraeli inkaona zimenezi mʼzigawo zonse za ulendo wawo.+