Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • nwt Ezra 1:1-10:44
  • Ezara

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ezara
  • Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Ezara

EZARA

1 Mʼchaka choyamba cha Koresi+ mfumu ya Perisiya, pokwaniritsa mawu a Yehova amene analankhula kudzera mwa Yeremiya,+ Yehova analimbikitsa Koresi mfumu ya Perisiya kuti alengeze mu ufumu wake wonse, zomwenso iye analemba mʼmakalata,+ kuti:

2 “Koresi mfumu ya Perisiya wanena kuti, ‘Yehova Mulungu wakumwamba wandipatsa maufumu onse apadziko lapansi.+ Iye wandituma kuti ndimumangire nyumba ku Yerusalemu+ mʼdziko la Yuda. 3 Aliyense amene ali pakati panu mwa anthu onse amene amamutumikira, Mulungu wake akhale naye ndipo apite ku Yerusalemu mʼdziko la Yuda nʼkukamanganso nyumba ya Yehova Mulungu wa Isiraeli. Iye ndi Mulungu woona ndipo nyumba yake inali ku Yerusalemu.* 4 Aliyense amene akukhala monga mlendo+ kulikonse, anthu oyandikana naye amuthandize pomupatsa siliva, golide, katundu, ziweto, limodzi ndi nsembe yaufulu ya nyumba ya Mulungu woona,+ yomwe inali ku Yerusalemu.’”

5 Ndiyeno atsogoleri a mabanja a fuko la Yuda, la Benjamini, ansembe, Alevi ndi aliyense amene Mulungu woona analimbikitsa mtima wake, anakonzeka kuti apite kukamanganso nyumba ya Yehova, yomwe inali ku Yerusalemu. 6 Anthu onse oyandikana nawo anawathandiza* powapatsa ziwiya zasiliva, zagolide, ziweto, zinthu zina zamtengo wapatali komanso katundu wosiyanasiyana, kuwonjezera pa zonse zimene zinaperekedwa mwaufulu.

7 Mfumu Koresi inabweretsanso ziwiya zamʼnyumba ya Yehova. Ziwiyazo nʼzimene Nebukadinezara anatenga ku Yerusalemu nʼkukaziika mʼkachisi wa mulungu wake.+ 8 Koresi mfumu ya Perisiya anatuma msungichuma Mitiredati kuti abweretse ziwiyazo nʼkuziwerenga. Atatero anazipereka kwa Sezibazara*+ mtsogoleri wa Yuda.

9 Ziwiyazo zinali zochuluka chonchi: ziwiya 30 zagolide zooneka ngati mabasiketi, ziwiya 1,000 zasiliva zooneka ngati mabasiketi ndi ziwiya 29 zowonjezera. 10 Panalinso mbale 30 zingʼonozingʼono zolowa zagolide, mbale 410 zingʼonozingʼono zolowa zasiliva zogwiritsira ntchito zina ndi ziwiya zina 1,000. 11 Ziwiya zonse zagolide ndi zasiliva zinalipo 5,400. Sezibazara anatenga zinthu zonsezi pamene anthu amene anagwidwa ukapolo+ ankachoka ku Babulo kupita ku Yerusalemu.

2 Awa ndi anthu amʼchigawo* amene anatuluka mu ukapolo+ pa anthu omwe Nebukadinezara mfumu ya ku Babulo anawatengera ku Babulo.+ Anthuwa anabwerera ku Yerusalemu ndi ku Yuda, aliyense kumzinda wakwawo.+ 2 Amenewa anabwera pamodzi ndi Zerubabele,+ Yesuwa,*+ Nehemiya, Seraya, Reelaya, Moredikayi, Bilisani, Misipara, Bigivai, Rehumu ndi Bana.

Chiwerengero cha amuna a Isiraeli chinali ichi:+ 3 Ana a Parosi, 2,172. 4 Ana a Sefatiya, 372. 5 Ana a Ara,+ 775. 6 Ana a Pahati-mowabu,+ ochokera mwa ana a Yesuwa ndi Yowabu, 2,812. 7 Ana a Elamu,+ 1,254. 8 Ana a Zatu,+ 945. 9 Ana a Zakai, 760. 10 Ana a Bani, 642. 11 Ana a Bebai, 623. 12 Ana a Azigadi, 1,222. 13 Ana a Adonikamu, 666. 14 Ana a Bigivai, 2,056. 15 Ana a Adini, 454. 16 Ana a Ateri, a mʼbanja la Hezekiya, 98. 17 Ana a Bezai, 323. 18 Ana a Yora, 112. 19 Ana a Hasumu,+ 223. 20 Ana a Gibara, 95. 21 Ana a Betelehemu, 123. 22 Amuna a ku Netofa, 56. 23 Amuna a ku Anatoti,+ 128. 24 Ana a Azimaveti, 42. 25 Ana a Kiriyati-yearimu, Kefira ndi Beeroti, 743. 26 Ana a Rama+ ndi Geba,+ 621. 27 Amuna a ku Mikemasi, 122. 28 Amuna a ku Beteli ndi a ku Ai,+ 223. 29 Ana a Nebo,+ 52. 30 Ana a Magabisi, 156. 31 Ana a Elamu wina, 1,254. 32 Ana a Harimu, 320. 33 Ana a Lodi, Hadidi ndi Ono, 725. 34 Ana a Yeriko, 345. 35 Ana a Senaya, 3,630.

36 Ansembe:+ Ana a Yedaya,+ a mʼbanja la Yesuwa,+ 973. 37 Ana a Imeri,+ 1,052. 38 Ana a Pasuri,+ 1,247. 39 Ana a Harimu,+ 1,017.

40 Alevi:+ Ana a Yesuwa, a mʼbanja la Kadimiyeli+ ochokera pakati pa ana a Hodaviya, 74. 41 Oimba,+ ana a Asafu,+ 128. 42 Ana a alonda apageti:+ ana a Salumu, ana a Ateri, ana a Talimoni,+ ana a Akubu,+ ana a Hatita ndi ana a Sobai, onse analipo 139.

43 Atumiki apakachisi:*+ Ana a Ziha, ana a Hasufa, ana a Tabaoti, 44 ana a Kerosi, ana a Siyaha, ana a Padoni, 45 ana a Lebana, ana a Hagaba, ana a Akubu, 46 ana a Hagabu, ana a Salimai, ana a Hanani, 47 ana a Gideli, ana a Gahara, ana a Reyaya, 48 ana a Rezini, ana a Nekoda, ana a Gazamu, 49 ana a Uziza, ana a Paseya, ana a Besai, 50 ana a Asena, ana a Meyuni, ana a Nefusimu, 51 ana a Bakibuki, ana a Hakufa, ana a Harihuri, 52 ana a Baziluti, ana a Mehida, ana a Harisa, 53 ana a Barikosi, ana a Sisera, ana a Tema, 54 ana a Neziya ndi ana a Hatifa.

55 Ana a atumiki a Solomo: Ana a Sotai, ana a Sofereti, ana a Peruda,+ 56 ana a Yaala, ana a Darikoni, ana a Gideli, 57 ana a Sefatiya, ana a Hatili, ana a Pokereti-hazebaimu ndi ana a Ami.

58 Atumiki onse apakachisi* pamodzi ndi ana a atumiki a Solomo analipo 392.

59 Amene anachokera ku Tele-mela, Tele-harisa, Kerubi, Adoni ndi Imeri, koma sanathe kufotokoza mzere wa makolo awo ndi kumene anachokera komanso kuti anali Aisiraeli kapena ayi, ndi awa:+ 60 ana a Delaya, ana a Tobia ndi ana a Nekoda, 652. 61 Ana a ansembe anali awa: ana a Habaya, ana a Hakozi,+ ana a Barizilai amene anatenga mkazi pakati pa ana aakazi a Barizilai+ wa ku Giliyadi nʼkuyamba kutchedwa ndi dzina lawo. 62 Amenewa ndi amene mayina awo anawayangʼana mʼkaundula kuti atsimikizire anthu onse za mzere wawo wobadwira koma sanapezekemo. Choncho anawaletsa kuti asatumikire ngati ansembe.*+ 63 Choncho, bwanamkubwa* anawauza kuti asamadye zinthu zopatulika koposa,+ mpaka patakhala wansembe amene angagwiritse ntchito Urimu ndi Tumimu.+

64 Anthu onse analipo 42,360.+ 65 Apa sanawerengere akapolo awo aamuna ndi aakazi amene analipo 7,337. Iwo analinso ndi oimba aamuna ndi aakazi okwana 200. 66 Anali ndi mahatchi* 736 ndi nyulu* 245. 67 Ngamila zawo zinalipo 435 ndipo abulu awo analipo 6,720.

68 Atsogoleri ena a nyumba za makolo awo atafika kunyumba ya Yehova imene inali ku Yerusalemu, anapereka zopereka zaufulu+ kunyumba ya Mulungu woona kuti imangidwenso pamalo ake.+ 69 Mogwirizana ndi chuma chawo, anapereka zinthu zoti zithandize pa ntchitoyo. Anapereka madalakima* agolide 61,000, ma mina*+ asiliva 5,000 ndi mikanjo 100 ya ansembe. 70 Ndiyeno ansembe, Alevi, anthu ena, oimba, alonda apageti, atumiki apakachisi* ndi Aisiraeli onse anayamba kukhala mʼmizinda yawo.+

3 Pofika mwezi wa 7,+ Aisiraeli omwe ankakhala mʼmizinda yawo anasonkhana limodzi mogwirizana ku Yerusalemu. 2 Kenako Yesuwa+ mwana wa Yehozadaki ndi ansembe anzake ndiponso Zerubabele+ mwana wa Salatiyeli+ ndi abale ake, anakamanga guwa lansembe la Mulungu wa Isiraeli. Anachita zimenezi kuti aziperekerapo nsembe zopsereza, mogwirizana ndi zimene zinalembedwa mʼChilamulo cha Mose,+ munthu wa Mulungu woona.

3 Iwo anamanga guwa lansembe pamalo ake akale ngakhale kuti ankaopa anthu a mitundu ina yowazungulira.+ Atatero anayamba kuperekerapo nsembe zopsereza kwa Yehova, zamʼmawa ndi zamadzulo.+ 4 Kenako anachita Chikondwerero cha Misasa mogwirizana ndi zimene zinalembedwa.+ Tsiku ndi tsiku ankapereka nsembe zopsereza zomwe zinkayenera kuperekedwa tsiku lililonse.+ 5 Ndiyeno anayamba kupereka nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku,+ nsembe ya masiku amene mwezi watsopano waoneka+ ndi nsembe za pa zikondwerero zopatulika+ za Yehova. Anaperekanso nsembe za aliyense amene anapereka chopereka chaufulu+ kwa Yehova ndi mtima wonse. 6 Kuyambira pa tsiku loyamba la mwezi wa 7+ kupita mʼtsogolo, anthuwo anayamba kupereka nsembe zopsereza kwa Yehova. Pa nthawiyi nʼkuti maziko a kachisi wa Yehova asanamangidwe.

7 Kenako anthuwo anapereka ndalama kwa anthu osema miyala+ ndi amisiri.+ Anaperekanso chakudya, zakumwa ndi mafuta kwa anthu a ku Sidoni ndi ku Turo chifukwa anabweretsa matabwa a mkungudza kudzera panyanja kuchokera ku Lebanoni kukafika ku Yopa.+ Anachita zimenezi mogwirizana ndi chilolezo chimene Koresi mfumu ya ku Perisiya anawapatsa.+

8 Mʼchaka chachiwiri kuchokera pamene anabwera kunyumba ya Mulungu woona ku Yerusalemu, mʼmwezi wachiwiri, Zerubabele mwana wa Salatiyeli, Yesuwa mwana wa Yehozadaki, abale awo onse, ansembe ndi Alevi ndiponso anthu ena onse amene anabwera ku Yerusalemu kuchokera ku ukapolo,+ anayamba kugwira ntchito. Anasankha Alevi oyambira zaka 20 kupita mʼtsogolo kuti akhale oyangʼanira ntchito yapanyumba ya Yehova. 9 Choncho Yesuwa, ana ake ndi abale ake, Kadimiyeli ndi ana ake, ndi ana a Yuda,* ananyamuka mogwirizana kuti akayangʼanire anthu ogwira ntchito mʼnyumba ya Mulungu woona. Panalinso ana a Henadadi,+ ana awo ndi abale awo, omwe anali Alevi.

10 Anthu amene ankamanga nyumbayo anamaliza kumanga maziko a kachisi wa Yehova.+ Atatero, ansembe ovala zovala zaunsembe omwe ananyamula malipenga+ ndiponso Alevi, ana a Asafu omwe ananyamula zinganga, anaimirira kuti atamande Yehova motsatira dongosolo limene Davide mfumu ya Isiraeli anakhazikitsa.+ 11 Iwo anayamba kuimba+ potamanda ndi kuyamika Yehova kuti, “iye ndi wabwino, chikondi chokhulupirika chimene amachisonyeza kwa Isiraeli chidzakhalapo mpaka kalekale.”+ Kenako anthu onse anafuula kwambiri potamanda Yehova chifukwa cha kumangidwa kwa maziko a nyumba ya Yehova. 12 Ansembe, Alevi ambiri ndi atsogoleri a nyumba za makolo awo, omwe anali amuna achikulire amene anaona nyumba yoyambirira,+ ankalira mokweza ataona maziko a nyumbayo pomwe ena ambiri ankafuula mosangalala.+ 13 Anthu ankalephera kusiyanitsa phokoso la chisangalalo ndi la kulira, chifukwa anthu osangalalawo ankafuula kwambiri, ndipo phokoso lawo linkamveka kutali kwambiri.

4 Adani a Yuda ndi Benjamini+ atamva kuti anthu amene anabwera kuchokera ku ukapolo+ akumangira kachisi Yehova Mulungu wa Isiraeli, 2 nthawi yomweyo anapita kwa Zerubabele ndi atsogoleri a nyumba za makolo nʼkukawauza kuti: “Bwanji tizimanga limodzi chifukwa ifeyo, mofanana ndi inuyo, timalambira* Mulungu wanu.+ Komanso timapereka nsembe kwa iye kuyambira mʼmasiku a Esari-hadoni+ mfumu ya Asuri, yemwe anatibweretsa kuno.”+ 3 Koma Zerubabele, Yesuwa ndi atsogoleri ena onse a nyumba za makolo za Isiraeli anawayankha kuti: “Sizingatheke kuti timange nyumba ya Mulungu wathu limodzi ndi inu.+ Timanga tokha nyumba ya Yehova Mulungu wa Isiraeli, mogwirizana ndi zimene Mfumu Koresi ya Perisiya yatilamula.”+

4 Kuyambira nthawi imeneyo, anthu amʼdzikolo anayamba kufooketsa* anthu a ku Yuda komanso kuwagwetsa ulesi kuti asapitirize ntchito yomanga.+ 5 Komanso, analemba ntchito alangizi kuti asokoneze mapulani awo+ pa nthawi yonse imene Koresi mfumu ya Perisiya ankalamulira, mpaka mu ulamuliro wa Dariyo+ mfumu ya Perisiya. 6 Kumayambiriro kwa ulamuliro wa Ahasiwero, iwo analemba kalata yonena zoipa zokhudza anthu a ku Yuda ndi ku Yerusalemu. 7 Mʼmasiku a Aritasasita mfumu ya Perisiya, Bisilamu, Mitiredati, Tabeeli ndi anzake ena onse analembera kalata mfumuyo. Kalatayo anaimasulira mʼChiaramu+ nʼkuilemba mʼzilembo za Chiaramu.*

8 * Rehumu mtsogoleri wa akuluakulu a boma ndi Simusai mlembi, analemba kalata yopita kwa mfumu Aritasasita yonena zoipa za anthu a ku Yerusalemu. Analemba kuti: 9 (Inachokera kwa Rehumu mtsogoleri wa akuluakulu a boma, Simusai mlembi, anzawo ena onse monga oweruza ndi abwanamkubwa aangʼono, alembi ena, anthu a ku Ereke,+ Ababulo, anthu a ku Susa,+ kapena kuti Aelamu,+ 10 mitundu ina yonse imene Asinapera wamkulu ndi wolemekezeka anaitenga kupita nayo ku ukapolo nʼkukaiika mʼmizinda ya ku Samariya+ ndi ena onse akutsidya lina la Mtsinje* . . . Tsopano 11 izi nʼzimene analemba mʼkalata imene anatumizayo.)

“Kwa mfumu Aritasasita, kuchokera kwa ife akapolo anu, amuna akutsidya lina la Mtsinje: Tsopano 12 inu mfumu dziwani kuti Ayuda amene anachokera kwa inu nʼkubwera kuno afika ku Yerusalemu. Iwo akumanganso mzinda woukira ndiponso woipa uja. Akumanganso mpanda+ komanso kukonza maziko. 13 Ndiyeno inu mfumu dziwani kuti, mzinda umenewu ukamangidwanso, mpanda wake nʼkumalizidwa, anthu amenewa asiya kupereka msonkho umene munthu aliyense amapereka, msonkho wakatundu+ ndi msonkho wamsewu ndipo zimenezi zidzachititsa kuti chuma cha mafumu chiwonongeke. 14 Tsopano popeza ife timalandira malipiro ochokera kunyumba yachifumu,* si bwino kuti tingolekerera kuti inu mfumu chuma chanu chiwonongeke. Choncho, tatumiza kalatayi kuti tikudziwitseni zimenezi inu mfumu 15 nʼcholinga choti mufufuze mʼbuku la mbiri ya makolo anu.+ Mukafufuza mʼbukulo mupeza kuti umenewu ndi mzinda woukira mafumu ndi zigawo za mayiko. Mumzinda umenewu mwakhala muli anthu oyambitsa kugalukira kuyambira kalekale. Nʼchifukwa chake mzindawu unawonongedwa.+ 16 Tikukudziwitsani mfumu kuti mzinda umenewu ukamangidwanso, mpanda wake nʼkumalizidwa, simudzalamuliranso kutsidya lino la Mtsinje.”+

17 Ndiyeno mfumuyo inatumiza uthenga kwa Rehumu mtsogoleri wa akuluakulu a boma, Simusai mlembi, anzawo ena onse amene ankakhala ku Samariya ndiponso kwa ena onse omwe ankakhala kutsidya lina la Mtsinje. Uthengawo unali wakuti:

“Moni! 18 Kalata imene mwatitumizira yawerengedwa* momveka bwino pamaso panga. 19 Choncho ine ndinalamula kuti afufuze, ndipo apeza kuti kuyambira kale mzinda umenewo wakhala ukuukira mafumu. Anthu amumzindawo akhala akuyambitsanso chisokonezo komanso kugalukira.+ 20 Mafumu amphamvu olamulira Yerusalemu ndi dera lonse la kutsidya lina la Mtsinje ankapatsidwa msonkho umene munthu aliyense amapereka, msonkho wakatundu komanso msonkho wamsewu. 21 Tsopano khazikitsani lamulo loti anthu amenewa asiye ntchitoyo kuti mzindawo usamangidwenso mpaka ine ndidzalamule. 22 Muonetsetse kuti musanyalanyaze kuchita zimenezi kuti vuto limeneli lisakule nʼkuwonongetsa chuma cha mfumu.”+

23 Mawu amene analembedwa mʼkalata ya mfumu Aritasasita anawerengedwa pamaso pa Rehumu, Simusai mlembi ndi anzawo. Kenako iwo anapita msangamsanga kwa Ayuda ku Yerusalemu nʼkukawaletsa ntchitoyo mwankhondo. 24 Pa nthawi imeneyi mʼpamene ntchito yomanga nyumba ya Mulungu, imene inali ku Yerusalemu, inaima ndipo inaima choncho mpaka chaka chachiwiri cha ulamuliro wa Dariyo mfumu ya Perisiya.+

5 Mneneri Hagai+ ndi mneneri Zekariya+ mdzukulu wa Ido,+ analosera kwa Ayuda a ku Yuda ndi ku Yerusalemu mʼdzina la Mulungu wa Isiraeli yemwe anali nawo. 2 Pa nthawi imeneyi ndi pamene Zerubabele+ mwana wa Salatiyeli ndi Yesuwa+ mwana wa Yehozadaki anayamba kumanganso nyumba ya Mulungu+ yomwe inali ku Yerusalemu. Aneneri a Mulungu anali nawo limodzi ndipo ankawathandiza.+ 3 Pa nthawi imeneyo Tatenai bwanamkubwa wa kutsidya lina la Mtsinje,* Setara-bozenai ndi anzawo anabwera kwa Ayudawo nʼkuwafunsa kuti: “Kodi ndi ndani wakulamulani kuti mumange nyumbayi komanso kumaliza ntchitoyi?”* 4 Anawafunsanso kuti: “Kodi anthu amene akumanga nyumba imeneyi mayina awo ndi ndani?” 5 Mulungu ankayangʼanira* akulu a Ayuda+ ndipo anthuwo sanawasiyitse ntchitoyo mpaka pamene analemba kalata yokhudza nkhaniyo nʼkuitumiza kwa Dariyo ndiponso pamene kalata yoyankha nkhaniyi inabwera.

6 Izi nʼzimene zinali mʼkalata imene Tatenai bwanamkubwa wa kutsidya lina la Mtsinje, Setara-bozenai ndi anzake ndiponso abwanamkubwa aangʼono amene anali kutsidya lina la Mtsinje, anatumiza kwa mfumu Dariyo. 7 Anatumiza uthenga kwa iye ndipo analemba kuti:

“Kwa Mfumu Dariyo:

Mtendere ukhale nanu. 8 Inu mfumu dziwani kuti ife tinapita kuchigawo cha Yuda kunyumba ya Mulungu wamkulu. Kumeneko takapeza kuti nyumbayo akuimanga ndi miyala yochita kugubuduza ndiponso akuika matabwa mʼmakoma ake. Iwo akugwira ntchitoyo mwakhama ndipo ikuyenda bwino. 9 Ndiyeno tinafunsa akuluakulu awo kuti: ‘Kodi ndi ndani wakulamulani kuti mumange nyumbayi komanso kumaliza ntchitoyi?’*+ 10 Tinawafunsanso mayina awo kuti tikuuzeni nʼcholinga choti tilembe mayina a anthu amene akuwatsogolera.

11 Iwo anatiyankha kuti: ‘Ndife atumiki a Mulungu wakumwamba ndi dziko lapansi. Tikumanganso nyumba imene inamangidwa zaka zambiri zapitazo, imene mfumu yaikulu ya Isiraeli inamanga nʼkuimaliza.+ 12 Koma chifukwa chakuti makolo athu anakwiyitsa Mulungu wakumwamba,+ iye anawapereka mʼmanja mwa Nebukadinezara+ mfumu ya Babulo Mkasidi, yemwe anagwetsa nyumbayi+ nʼkutenga anthu kupita nawo ku ukapolo ku Babulo.+ 13 Koma mʼchaka choyamba cha Koresi mfumu ya Babulo, mfumu Koresi inaika lamulo loti nyumba ya Mulunguyi imangidwenso.+ 14 Komanso, mfumu Koresi inachotsa mʼkachisi wa ku Babulo ziwiya zagolide ndi zasiliva zimene Nebukadinezara anazitenga mʼkachisi wa Mulungu yemwe anali ku Yerusalemu, nʼkupita nazo kukachisi wa ku Babuloyo.+ Ndiyeno anazipereka kwa munthu wina dzina lake Sezibazara,*+ amene Koresi anamusankha kuti akhale bwanamkubwa.+ 15 Koresiyo anamuuza kuti: “Tenga ziwiyazi, ukaziike mʼkachisi amene ali ku Yerusalemu. Ukaonetsetse kuti nyumba ya Mulungu yamangidwanso pamalo ake.”+ 16 Sezibazarayo atabwera anamanga maziko a nyumba ya Mulungu+ yomwe ili ku Yerusalemu. Kuyambira nthawi imeneyo mpaka pano nyumbayi ikumangidwabe ndipo sinamalizidwe.’+

17 Tsopano ngati inu mfumu mukuona kuti nʼkoyenera, uzani anthu kuti afufuze mʼnyumba ya chuma cha mfumu imene ili ku Babuloko. Muwauze kuti aone ngati mfumu Koresi inaikadi lamulo loti nyumba ya Mulungu yomwe ili ku Yerusalemu+ imangidwenso. Kenako inu mfumu mutitumizire chigamulo chanu pa nkhani imeneyi.”

6 Pa nthawiyi mʼpamene mfumu Dariyo inaika lamulo loti afufuze mʼnyumba yosungiramo zinthu zakale, momwe ankasungamonso zinthu zamtengo wapatali zimene zinapititsidwa ku Babulo. 2 Kumalo okhala ndi mpanda wolimba kwambiri a ku Ekibatana, mʼchigawo cha dziko la Amedi, anapezako mpukutu. Mumpukutuwo munalembedwa uthenga wakuti:

3 “Mʼchaka choyamba cha Mfumu Koresi, mfumuyo inaika lamulo lokhudza nyumba ya Mulungu ku Yerusalemu lakuti:+ ‘Ayuda amangenso nyumbayo kuti azikapereka nsembe kumeneko ndipo amange maziko olimba. Nyumbayo ikhale mikono 60* kupita mʼmwamba ndiponso mikono 60 mulifupi mwake.+ 4 Ikhale ndi mizere itatu yamiyala ikuluikulu yochita kugubuduza komanso mzere umodzi wa matabwa.+ Ndalama zake zichokere kunyumba ya mfumu.+ 5 Ziwiya zagolide ndi zasiliva za mʼnyumba ya Mulungu, zimene Nebukadinezara anatenga mʼkachisi yemwe anali ku Yerusalemu nʼkuzipititsa ku Babulo,+ zibwezedwe kuti zikaikidwe kumalo ake, kukachisi amene ali ku Yerusalemu ndipo zikaikidwe mʼnyumba ya Mulungu.’+

6 Tsopano inu Tatenai bwanamkubwa wa kutsidya lina la Mtsinje,* Setara-bozenai ndi anzanu ndiponso abwanamkubwa aangʼono amene ali kutsidya lina la Mtsinje,+ musapite kumeneko. 7 Musakasokoneze ntchito yomanga nyumba ya Mulungu. Bwanamkubwa wa Ayuda ndi akuluakulu a Ayuda amanganso nyumba ya Mulunguyo pamalo ake. 8 Ndaikanso lamulo lokhudza zimene muyenera kuchita ndi akuluakulu a Ayuda amenewa pa ntchito yomanganso nyumba ya Mulungu. Amuna amenewa muziwapatsa ndalama zochokera pa chuma cha mfumu+ zomwe anthu a kutsidya la Mtsinje amapereka pokhoma msonkho kuti ntchitoyo isaime.+ 9 Komanso muziwapatsa zinthu zomwe akufunikira monga ngʼombe zingʼonozingʼono zamphongo,+ nkhosa zamphongo+ ndi ana a nkhosa+ kuti azipereka nsembe yopsereza kwa Mulungu wakumwamba. Muziwapatsanso tirigu,+ mchere,+ vinyo+ ndi mafuta+ mogwirizana ndi zimene ansembe amene ali ku Yerusalemu anganene. Muziwapatsa zinthu zimenezi tsiku ndi tsiku 10 kuti nthawi zonse azipereka nsembe zosangalatsa Mulungu wakumwamba ndiponso kuti azipempherera mfumu ndi ana ake kuti akhale ndi moyo wabwino.+ 11 Ndaikanso lamulo lakuti aliyense wophwanya lamulo limeneli, thabwa* lidzachotsedwe panyumba yake ndipo iye adzapachikidwe pathabwalo. Komanso nyumba yake idzasandutsidwa chimbudzi* cha aliyense chifukwa cha zimenezi. 12 Mulungu amene anaika dzina lake kumeneko,+ achotse mfumu iliyonse ndi anthu alionse ophwanya lamulo limeneli ndiponso owononga nyumba ya Mulungu imene ili ku Yerusalemu. Ine Dariyo ndaika lamulo limeneli, ndipo zichitike mwamsanga.”

13 Kenako Tatenai bwanamkubwa wa kutsidya lina la Mtsinje, Setara-bozenai+ ndi anzawo anachita zimenezi mwamsanga mogwirizana ndi mawu amene mfumu Dariyo inatumiza. 14 Tsopano akuluakulu a Ayuda anapitiriza kumanga ndipo ntchitoyo inkayenda bwino+ chifukwa cholimbikitsidwa ndi ulosi wa mneneri Hagai+ ndi Zekariya+ mdzukulu wa Ido. Iwo anamanga nyumbayo nʼkuimaliza potsatira lamulo la Mulungu wa Isiraeli+ ndi lamulo la Koresi,+ Dariyo+ komanso Aritasasita mfumu ya Perisiya.+ 15 Iwo anamaliza nyumbayo pa tsiku lachitatu la mwezi wa Adara,* mʼchaka cha 6 cha ulamuliro wa Mfumu Dariyo.

16 Ndiyeno Aisiraeli, ansembe, Alevi+ ndi anthu ena onse amene anachokera ku ukapolo, anatsegulira nyumba ya Mulunguyo mosangalala. 17 Iwo anapereka nsembe ngʼombe zamphongo 100, nkhosa zamphongo 200 ndi ana a nkhosa amphongo 400. Anaperekanso mbuzi zamphongo 12 za nsembe yamachimo ya Aisiraeli onse, mogwirizana ndi chiwerengero cha mafuko a Isiraeli.+ 18 Kenako anaika ansembe ndi Alevi mʼmagulu awo kuti azitumikira Mulungu ku Yerusalemu+ mogwirizana ndi malangizo a mʼbuku la Mose.+

19 Anthu amene anachokera ku ukapolowo anachita Pasika pa tsiku la 14 la mwezi woyamba.+ 20 Chifukwa chakuti ansembe ndi Alevi anadziyeretsa+ ndipo palibe anatsala, onse anali oyera. Choncho Aleviwo anapha nyama ya Pasika ya anthu onse amene anachokera ku ukapolo, ya abale awo ansembe ndiponso yawo. 21 Ndiyeno Aisiraeli amene anabwera kuchokera ku ukapolo anadya nyamayo. Komanso aliyense amene anadzilekanitsa ku zonyansa za anthu a mitundu yamʼdzikolo nʼkubwera kwa iwo kuti alambire* Yehova Mulungu wa Isiraeli, anadya nawo.+ 22 Kwa masiku 7, iwo anachita Chikondwerero cha Mikate Yopanda Zofufumitsa+ mosangalala chifukwa Yehova anawachititsa kuti asangalale. Iye anachititsa kuti mfumu ya Asuri iwakomere mtima+ nʼkuwathandiza* pa ntchito yomanga nyumba ya Mulungu woona, Mulungu wa Isiraeli.

7 Zimenezi zitachitika, mu ulamuliro wa mfumu Aritasasita+ ya ku Perisiya, Ezara*+ anabwera ku Yerusalemu kuchokera ku Babulo. Iye anali mwana wa Seraya.+ Seraya anali mwana wa Azariya, Azariya anali mwana wa Hilikiya,+ 2 Hilikiya anali mwana wa Salumu, Salumu anali mwana wa Zadoki, Zadoki anali mwana wa Ahitubu, 3 Ahitubu anali mwana wa Amariya, Amariya anali mwana wa Azariya,+ Azariya anali mwana wa Merayoti, 4 Merayoti anali mwana wa Zerahiya, Zerahiya anali mwana wa Uzi, Uzi anali mwana wa Buki, 5 Buki anali mwana wa Abisuwa, Abisuwa anali mwana wa Pinihasi,+ Pinihasi anali mwana wa Eliezara+ ndipo Eliezara anali mwana wa Aroni+ wansembe wamkulu. 6 Ezara anabwera kuchokera ku Babulo. Iye anali wokopera* Malemba ndipo ankadziwa bwino* Chilamulo cha Mose+ chimene Yehova Mulungu wa Isiraeli anapereka. Mfumu inamupatsa zonse zimene anapempha chifukwa dzanja la Yehova Mulungu wake linkamuthandiza.

7 Ena mwa Aisiraeli, ansembe, Alevi,+ oimba,+ alonda apageti+ ndi atumiki apakachisi*+ anapita ku Yerusalemu mʼchaka cha 7 cha mfumu Aritasasita. 8 Ezara anabwera ku Yerusalemu mʼmwezi wa 5, mʼchaka cha 7 cha mfumuyo. 9 Pa tsiku loyamba la mwezi woyamba, iye ananyamuka kuchokera ku Babulo ndipo anafika ku Yerusalemu pa tsiku loyamba la mwezi wa 5. Iye anafika ku Yerusalemu chifukwa dzanja labwino la Mulungu wake linkamuthandiza.+ 10 Ezara anakonzekeretsa mtima wake* kuti aphunzire Chilamulo cha Yehova, azichigwiritsa ntchito+ komanso kuti aziphunzitsa malamulo ndi ziweruzo mu Isiraeli.+

11 Izi nʼzimene zinali mʼkalata imene Mfumu Aritasasita inapereka kwa wansembe Ezara wokopera Malemba,* katswiri pophunzira* malamulo a Yehova ndi malangizo amene anapereka kwa Aisiraeli:

12 * “Kuchokera kwa Aritasasita,+ mfumu ya mafumu, kupita kwa wansembe Ezara, wokopera* Chilamulo cha Mulungu wakumwamba: Mtendere ukhale nawe. Tsopano 13 ndaika lamulo lakuti aliyense mu ufumu wanga pakati pa anthu a Isiraeli, ansembe awo ndi Alevi amene akufuna kupita nawe ku Yerusalemu apite.+ 14 Iwe watumizidwa ndi mfumu komanso alangizi ake 7 kuti ukafufuze ngati anthu a ku Yuda ndi ku Yerusalemu akutsatira Chilamulo cha Mulungu wako, chimene uli nacho.* 15 Utenge siliva ndi golide zimene mfumu ndi alangizi ake apereka mwakufuna kwawo kwa Mulungu wa Isiraeli, amene amakhala ku Yerusalemu. 16 Utengenso siliva ndi golide yense amene ulandire* mʼchigawo chonse cha Babulo, limodzi ndi mphatso za anthu komanso za ansembe omwe akupereka mwakufuna kwawo kunyumba ya Mulungu wawo, yomwe ili ku Yerusalemu.+ 17 Ndalamazi ukagulire mwamsangamsanga ngʼombe zamphongo,+ nkhosa zamphongo,+ ana a nkhosa,+ limodzi ndi nsembe zake zambewu+ ndiponso nsembe zake zachakumwa.+ Zimenezi ukazipereke paguwa lansembe lapanyumba ya Mulungu wako, yomwe ili ku Yerusalemu.

18 Zilizonse zimene iweyo ndi abale ako mudzaone kuti nʼzabwino kuchita ndi siliva ndi golide wotsala, mogwirizana ndi zimene Mulungu wanu akufuna, mudzachite zimenezo. 19 Ziwiya zimene wapatsidwa kuti zikagwiritsidwe ntchito pa utumiki wapanyumba ya Mulungu wako, ukaziike pamaso pa Mulungu ku Yerusalemu.+ 20 Zinthu zina zonse zofunika panyumba ya Mulungu wako zimene ukuyenera kupereka, ukazitenge kunyumba yosungiramo chuma cha mfumu.+

21 Ineyo mfumu Aritasasita ndalamula asungichuma onse amene ali kutsidya lina la Mtsinje,* kuti chilichonse chimene wansembe Ezara,+ wokopera* Chilamulo cha Mulungu wakumwamba, angapemphe kwa inu chichitidwe mwamsanga. 22 Mumʼpatse ngakhale matalente* 100 a siliva, miyezo ya kori* 100 ya tirigu, mitsuko* 100 ya vinyo,+ mitsuko 100 ya mafuta+ ndi mchere+ wambiri. 23 Zonse zimene Mulungu wakumwamba walamula zokhudza nyumba yake, zichitidwe ndi mtima wonse+ kuti asakwiyire kwambiri ineyo, ana anga ndi anthu anga.+ 24 Ndikufuna kukuuzaninso kuti si zololeka kulandira msonkho kuchokera kwa ansembe, Alevi, oimba,+ alonda apakhomo, atumiki a pakachisi*+ ndi anthu ogwira ntchito panyumba ya Mulungu. Musawakhometse msonkho umene munthu aliyense amakhoma, msonkho wakatundu+ komanso msonkho wamsewu.

25 Iweyo Ezara, pogwiritsa ntchito nzeru zimene Mulungu wako wakupatsa,* uike akuluakulu a zamalamulo ndi oweruza kuti nthawi zonse aziweruza anthu onse akutsidya la Mtsinje komanso onse odziwa malamulo a Mulungu wako. Aliyense amene sadziwa malamulowo, uzimuphunzitsa.+ 26 Aliyense wosatsatira Chilamulo cha Mulungu wako ndi lamulo la mfumu, azipatsidwa chiweruzo msangamsanga, kaya choti aphedwe, athamangitsidwe, alipitsidwe kapena aikidwe mʼndende.”

27 Atamandike Yehova Mulungu wa makolo athu, amene waika maganizo amenewa mumtima mwa mfumu, kuti nyumba ya Yehova imene ili ku Yerusalemu ikongoletsedwe.+ 28 Iye wandisonyeza chikondi chokhulupirika pamaso pa mfumu,+ pamaso pa alangizi ake+ ndiponso pamaso pa akalonga onse amphamvu a mfumu. Ineyo ndinalimba mtima* chifukwa dzanja la Yehova Mulungu wanga linkandithandiza, ndipo ndinasonkhanitsa atsogoleri a Aisiraeli kuti tipitire limodzi.

8 Awa ndi mayina a atsogoleri a nyumba za makolo awo komanso mndandanda wa mayina wotsatira makolo a anthu amene ndinachoka nawo ku Babulo, mu ulamuliro wa Mfumu Aritasasita:+ 2 Pa ana a Pinihasi+ panali Gerisomu, pa ana a Itamara+ panali Danieli, pa ana a Davide panali Hatusi. 3 Pa ana a Sekaniya panali Zekariya wochokera kwa ana a Parosi. Iye anali ndi amuna amene analembetsa mayina awo okwana 150. 4 Pa ana a Pahati-mowabu+ panali Eliho-enai mwana wa Zerahiya. Iye anali ndi amuna 200. 5 Pa ana a Zatu+ panali Sekaniya mwana wa Yahazieli. Iye anali ndi amuna 300. 6 Pa ana a Adini+ panali Ebedi mwana wa Yonatani. Iye anali ndi amuna 50. 7 Pa ana a Elamu+ panali Yesaiya mwana wa Ataliya. Iye anali ndi amuna 70. 8 Pa ana a Sefatiya+ panali Zebadiya mwana wa Mikayeli. Iye anali ndi amuna 80. 9 Pa ana a Yowabu panali Obadiya mwana wa Yehiela. Iye anali ndi amuna 218. 10 Pa ana a Bani panali Selomiti mwana wa Yosifiya. Iye anali ndi amuna 160. 11 Pa ana a Bebai+ panali Zekariya mwana wa Bebai. Iye anali ndi amuna 28. 12 Pa ana a Azigadi+ panali Yohanani mwana wa Hakatani. Iye anali ndi amuna 110. 13 Pa ana a Adonikamu,+ omwe anali omaliza, panali anthu awa: Elifeleti, Yeyeli ndi Semaya. Iwo anali ndi amuna 60. 14 Pa ana a Bigivai+ panali Utai ndi Zabudi. Iwo anali ndi amuna 70.

15 Ndinawasonkhanitsa pamtsinje umene umafika ku Ahava+ ndipo tinamanga msasa pamenepo nʼkukhalapo masiku atatu. Koma nditafufuza bwinobwino anthuwo komanso ansembe, sindinapezepo Alevi. 16 Choncho ndinaitanitsa Eliezere, Ariyeli, Semaya, Elinatani, Yaribi, Elinatani, Natani, Zekariya ndi Mesulamu, omwe anali atsogoleri awo. Ndinaitanitsanso Yoyaribi ndi Elinatani, omwe anali alangizi. 17 Kenako ndinawalamula kuti apite kwa Ido yemwe anali mtsogoleri pamalo otchedwa Kasifiya. Ndinawauza mawu oti akauze Ido ndi abale ake, atumiki apakachisi* omwe anali ku Kasifiyako kuti atibweretsere atumiki apanyumba ya Mulungu wathu. 18 Popeza dzanja labwino la Mulungu wathu linkatithandiza, iwo anatibweretsera munthu wanzeru wochokera pakati pa ana a Mali+ mdzukulu wa Levi mwana wa Isiraeli. Dzina lake linali Serebiya+ ndipo anabwera limodzi ndi ana ake komanso abale ake. Onse pamodzi analipo 18. 19 Panalinso Hasabiya, yemwe anali pamodzi ndi Yesaiya wochokera pa ana a Merari,+ abale ake ndi ana awo. Onse pamodzi analipo 20. 20 Kuchokera pa atumiki apakachisi* amene Davide ndi akalonga anawaika kuti azitumikira Alevi, panali atumiki a pakachisi 220. Onsewa anawasankha pochita kuwatchula mayina awo.

21 Kenako ndinalamula kuti tisale kudya tili kumtsinje wa Ahava komweko, kuti tidzichepetse pamaso pa Mulungu wathu nʼkumupempha kuti atitsogolere pa ulendo wathu, pamodzi ndi ana athu ndi katundu wathu yense. 22 Ndinachita manyazi kupempha asilikali kwa mfumu ndi okwera pamahatchi kuti atiteteze kwa adani mʼnjira, chifukwa tinali titauza mfumuyo kuti: “Dzanja labwino la Mulungu wathu limathandiza anthu onse omufunafuna,+ koma amasonyeza mkwiyo ndi mphamvu zake kwa onse omusiya.”+ 23 Choncho tinasala kudya nʼkupempha Mulungu wathu zimenezi ndipo iye anamva pempho lathu.+

24 Tsopano ndaika padera anthu 12 kuchokera pa atsogoleri a ansembe. Mayina awo ndi Serebiya komanso Hasabiya+ pamodzi ndi abale awo 10. 25 Ndiyeno ndinawayezera siliva, golide ndi ziwiya. Zimenezi zinali zopereka zimene mfumu, alangizi ake, akalonga ake ndi Aisiraeli onse amene anali kumeneko anapereka kunyumba ya Mulungu wathu.+ 26 Chotero ndinawayezera nʼkuwapatsa matalente* 650 a siliva, ziwiya 100 zasiliva zokwana matalente awiri, matalente 100 a golide, 27 mbale 20 zingʼonozingʼono zagolide zolowa zokwana madariki* 1,000 ndi ziwiya ziwiri zamkuwa wabwino wonyezimira mofiirira, zamtengo wapatali ngati golide.

28 Kenako ndinawauza kuti: “Inu ndinu oyera kwa Yehova.+ Ziwiyazi ndi zopatulika ndipo siliva komanso golideyu ndi nsembe yaufulu yopita kwa Yehova Mulungu wa makolo anu. 29 Muyangʼanire katunduyu mosamala mpaka atayezedwa pamaso pa atsogoleri a ansembe, atsogoleri a Alevi komanso akalonga a nyumba zamakolo a Aisiraeli ku Yerusalemu,+ mʼzipinda zodyera zapanyumba ya Yehova.” 30 Ansembe ndi Aleviwo analandira siliva ndi golide amene anayezedwayo ndiponso ziwiya zimene zinayezedwazo, kuti apititse zinthuzi ku Yerusalemu kunyumba ya Mulungu wathu.

31 Kenako tinachoka pamtsinje wa Ahava+ pa tsiku la 12 la mwezi woyamba+ kupita ku Yerusalemu. Dzanja la Mulungu wathu linkatithandiza pa ulendowu moti anatipulumutsa kwa adani ndiponso achifwamba mʼnjira. 32 Kenako tinafika ku Yerusalemu+ ndipo tinakhala kumeneko masiku atatu. 33 Pa tsiku la 4 tinayeza siliva, golide ndi ziwiya zija mʼnyumba ya Mulungu wathu.+ Titatero tinapereka zinthuzo kwa Meremoti+ mwana wa Uliya wansembe, yemwe anali limodzi ndi Eliezara mwana wa Pinihasi. Analinso limodzi ndi Yozabadi+ mwana wa Yesuwa ndi Nowadiya mwana wa Binui,+ omwe anali Alevi. 34 Zinthu zonsezo tinaziwerenga nʼkuziyeza, kenako tinalemba kulemera kwake. 35 Anthu amene anali ku ukapolo mʼdziko lina anapereka nsembe zopsereza kwa Mulungu wa Isiraeli. Anapereka ngʼombe zamphongo 12+ za Aisiraeli onse, nkhosa zamphongo 96,+ ana a nkhosa amphongo 77 ndi mbuzi zamphongo 12+ kuti zikhale nsembe yamachimo. Zonsezi anazipereka kuti zikhale nsembe zopsereza kwa Yehova.+

36 Kenako tinapereka malamulo a mfumu+ kwa masatarapi* a mfumu ndi abwanamkubwa a kutsidya lina la Mtsinje.*+ Malamulowo anathandiza anthuwo ndiponso anathandiza panyumba ya Mulungu woona.+

9 Zimenezi zitangotha, akalonga anabwera kwa ine nʼkundiuza kuti: “Aisiraeli, ansembe ndiponso Alevi sanadzipatule kwa anthu a mitundu ina komanso ku zonyansa za mitunduyo.+ Anthu ake ndi Akanani, Ahiti, Aperezi, Ayebusi, Aamoni, Amowabu, Aiguputo+ ndi Aamori.+ 2 Iwo atenga ena mwa ana aakazi a mitundu inayo kuti akhale akazi awo ndi akazi a ana awo aamuna.+ Anthuwa, omwe ndi ana* opatulika,+ asakanikirana ndi anthu a mitundu ina.+ Akalonga komanso atsogoleri ndi amene ali patsogolo kuchita zosakhulupirikazi.”

3 Nditangomva nkhaniyi, ndinangʼamba zovala zanga nʼkuzula tsitsi langa ndi ndevu zanga, ndipo ndinakhala pansi nditakhumudwa kwambiri. 4 Aliyense amene ankalemekeza mawu a Mulungu wa Isiraeli anabwera nʼkundizungulira chifukwa cha kusakhulupirika kwa anthu amene anachokera ku ukapolo. Pa nthawiyi nʼkuti ndili wokhumudwa kwambiri ndipo ndinakhala pansi mpaka nthawi yopereka nsembe yambewu yamadzulo.+

5 Pa nthawi yopereka nsembe yambewu yamadzulo,+ ndinaimirira mwamanyazi, zovala zanga zili zongʼambika ndipo ndinagwada nʼkukweza manja anga kwa Yehova Mulungu wanga. 6 Kenako ndinanena kuti: “Inu Mulungu wanga, ndikuchita manyazi kuti ndikweze nkhope yanga kuyangʼana kwa inu Mulungu wanga, chifukwa zolakwa zathu zachuluka kupitirira pamutu pathu ndipo machimo athu aunjikana mpaka kumwamba.+ 7 Kuyambira masiku a makolo athu mpaka lero machimo athu achuluka.+ Chifukwa cha zolakwa zathu, ifeyo, mafumu athu ndi ansembe athu, taperekedwa mʼmanja mwa mafumu a mayiko ena, taphedwa ndi lupanga,+ tatengedwa kupita ku ukapolo,+ talandidwa katundu+ komanso takhala amanyazi ngati mmene tilili lero.+ 8 Koma kwa nthawi yochepa, Yehova Mulungu wathu watikomera mtima polola anthu ena kuti apulumuke ndipo watipatsa malo otetezeka* mʼmalo ake oyera+ kuti maso athu awale. Mulungu wathu watitsitsimula pangʼono mu ukapolo wathu. 9 Ngakhale kuti ndife akapolo,+ Mulungu wathu sanatisiye mu ukapolo wathuwo, koma watisonyeza chikondi chokhulupirika pamaso pa mafumu a ku Perisiya.+ Wachita zimenezi kuti atitsitsimutse nʼcholinga choti tikamangenso nyumba ya Mulungu wathu+ komanso tikakonze malo ozungulira nyumbayo amene anawonongedwa, ndiponso kuti tikhale mu Yuda ndi mu Yerusalemu ngati kuti tili mumpanda wamiyala.*

10 Ndiyeno tinganene chiyani inu Mulungu wathu pambuyo pa zimene zachitikazi? Popeza tasiya malamulo anu 11 amene munatilamula kudzera mwa atumiki anu aneneri, akuti, ‘Dziko limene mukukalitenga kuti likhale lanu ndi lodetsedwa chifukwa anthu ake ndi odetsedwa ndi zonyansa zawo zimene adzaza nazo dziko lonselo.+ 12 Choncho musakapereke ana anu aakazi kwa ana awo aamuna, kapena kutenga ana awo aakazi nʼkuwapereka kwa ana anu aamuna.+ Musakalole kuti akhale pamtendere ndiponso kuti atukuke.+ Mukachite zimenezi kuti mukakhale amphamvu, mukadye zabwino zamʼdzikolo ndiponso kuti mukalitenge kuti likhale la ana anu mpaka kalekale.’ 13 Pambuyo pa zonse zimene zatigwera chifukwa cha zochita zathu zoipa ndi machimo athu ochuluka, ndipo inu Mulungu wathu simunatilange mogwirizana ndi kulakwa kwathu+ komanso mwalola kuti enafe tipulumuke,+ 14 kodi zoona tiphwanyenso malamulo anu kachiwiri pokwatirana ndi anthu a mitundu ina omwe amachita zonyansawa?+ Kodi tikatero simutikwiyira koopsa nʼkupezeka kuti sipanatsalenso wina wopulumuka? 15 Inu Yehova Mulungu wa Isiraeli ndinu wolungama+ chifukwa ife tidakali ndi moyo mpaka lero. Taima pamaso panu mʼmachimo athu, ngakhale kuti nʼzosatheka kuima pamaso panu chifukwa cha zimenezi.”+

10 Pamene Ezara ankapemphera+ komanso kuvomereza machimo, zomwe ankachita akulira ndiponso atagona patsogolo pa nyumba ya Mulungu woona, gulu lalikulu la Aisiraeli linamuzungulira. Panali amuna, akazi ndi ana ndipo ankalira kwambiri. 2 Kenako Sekaniya mwana wa Yehiela+ wochokera mwa ana a Elamu+ anauza Ezara kuti: “Ifeyo tachita zosakhulupirika kwa Mulungu wathu chifukwa tinakwatira akazi achilendo kuchokera kwa anthu a mitundu ina.+ Ngakhale zili choncho, Aisiraeli ali ndi chiyembekezo. 3 Tsopano tiyeni tichite pangano ndi Mulungu wathu,+ kuti tisiya akazi onsewa komanso ana awo mogwirizana ndi lamulo la Yehova ndiponso anthu amene amalemekeza lamulo la Mulungu.+ Tiyeni tichite zinthu mogwirizana ndi Chilamulo. 4 Choncho dzuka, chifukwa nkhaniyi ili mʼmanja mwako ndipo ife tili nawe. Uchite zinthu mwamphamvu.”

5 Choncho Ezara ananyamuka nʼkuuza atsogoleri a ansembe, a Alevi ndi a Aisiraeli onse kuti alumbire kuti achita mogwirizana ndi zimene ananena+ ndipo analumbiradi. 6 Kenako Ezara anachoka panyumba ya Mulungu woona nʼkupita kuchipinda chodyera cha Yehohanani mwana wa Eliyasibu. Ngakhale kuti anapita kumeneko, sanadye chakudya kapena kumwa madzi, popeza ankalira chifukwa cha kusakhulupirika kwa anthu ochokera ku ukapolo aja.+

7 Ndiyeno analengeza ku Yuda ndi ku Yerusalemu konse kuti anthu onse amene anachokera ku ukapolo asonkhane ku Yerusalemu, 8 ndipo mogwirizana ndi lamulo la akalonga ndi akulu, aliyense amene sabwera pakapita masiku atatu, katundu wake yense alandidwa ndipo iyeyo achotsedwa pa gulu la anthu amene anachokera ku ukapolo.+ 9 Choncho pasanathe masiku atatu, amuna onse a fuko la Yuda ndi la Benjamini anasonkhana ku Yerusalemu. Zimenezi zinachitika pa tsiku la 20 la mwezi wa 9. Anthu onsewo anakhala pabwalo la nyumba ya Mulungu woona, akunjenjemera chifukwa cha nkhaniyo komanso chifukwa kunkagwa mvula yambiri.

10 Kenako wansembe Ezara anaimirira nʼkuuza anthuwo kuti: “Inu mwachita zosakhulupirika chifukwa mwatenga akazi achilendo+ ndipo mwawonjezera machimo a Isiraeli. 11 Choncho vomerezani machimo anu kwa Yehova Mulungu wa makolo anu ndipo chitani zomusangalatsa. Musiyane ndi anthu a mitundu ina ndiponso akazi achilendowa.”+ 12 Gulu lonselo linayankha mokweza kuti: “Tichita ndendende mogwirizana ndi zimene mwanena. 13 Koma tilipo anthu ambiri ndipo ino ndi nyengo ya mvula, choncho nʼzosatheka kuima panja. Komanso nkhani imeneyi sitenga tsiku limodzi kapena masiku awiri chifukwa tachimwa kwambiri. 14 Choncho lolani kuti akalonga athu aimire anthu onse+ ndipo aliyense mʼmizinda yathu, amene wakwatira mkazi wachilendo, abwere pa nthawi imene ikhazikitsidwe. Abwere limodzi ndi akulu a mzinda uliwonse ndi oweruza ake, mpaka titabweza mkwiyo wa Mulungu wathu amene watikwiyira kwambiri chifukwa cha nkhani imeneyi.”

15 Koma Yonatani mwana wa Asaheli ndi Yahazeya mwana wa Tikiva anatsutsa zimenezi, ndipo Mesulamu ndi Sabetai,+ omwe anali Alevi, anawathandiza. 16 Anthu amene anachokera ku ukapolowo anachita zimene anagwirizanazo. Choncho wansembe Ezara ndi amuna onse amene anali atsogoleri a nyumba za makolo awo, omwe anachita kuwatchula mayina awo, anachoka pakati pa anthuwo nʼkukakhala pansi kuti afufuze nkhaniyo. Anachita zimenezi pa tsiku loyamba la mwezi wa 10. 17 Pofika tsiku loyamba la mwezi woyamba, anathetsa nkhani zonse zokhudza amuna amene anatenga akazi achilendo. 18 Iwo anapeza kuti ana ena a ansembe anakwatira akazi achilendo.+ Kuchokera pa ana a Yesuwa+ mwana wa Yehozadaki ndi abale ake, panali Maaseya, Eliezere, Yaribi ndi Gedaliya. 19 Koma iwo analonjeza kuti asiya akazi awo komanso popeza anachimwa, apereka nkhosa yamphongo chifukwa cha tchimo lawolo.+

20 Pa ana a Imeri+ panali Haneni ndi Zebadiya. 21 Pa ana a Harimu+ panali Maaseya, Eliya, Semaya, Yehiela ndi Uziya. 22 Pa ana a Pasuri+ panali Elioenai, Maaseya, Isimaeli, Netaneli, Yozabadi ndi Eleasa. 23 Pa Alevi panali Yozabadi, Simeyi, Kelaya (kapena kuti Kelita), Petahiya, Yuda ndi Eliezere. 24 Pa oimba panali Eliyasibu. Pa alonda apageti panali Salumu, Telemu ndi Uri.

25 Kuchokera pa Aisiraeli, pa ana a Parosi+ panali Ramiya, Iziya, Malikiya, Miyamini, Eliezara, Malikiya ndi Benaya. 26 Pa ana a Elamu+ panali Mataniya, Zekariya, Yehiela,+ Abidi, Yeremoti ndi Eliya. 27 Pa ana a Zatu+ panali Elioenai, Eliyasibu, Mataniya, Yeremoti, Zabadi ndi Aziza. 28 Pa ana a Bebai+ panali Yehohanani, Hananiya, Zabai ndi Atilai. 29 Pa ana a Bani panali Mesulamu, Maluki, Adaya, Yasubi, Seali ndi Yeremoti. 30 Pa ana a Pahati-mowabu+ panali Adena, Kelali, Benaya, Maaseya, Mataniya, Bezaleli, Binui ndi Manase. 31 Pa ana a Harimu+ panali Eliezere, Isihiya, Malikiya,+ Semaya, Simeoni, 32 Benjamini, Maluki ndi Semariya. 33 Pa ana a Hasumu+ panali Matenai, Mateta, Zabadi, Elifeleti, Yeremai, Manase ndi Simeyi. 34 Pa ana a Bani panali Maadai, Amuramu, Ueli, 35 Benaya, Bedeya, Kelui, 36 Vaniya, Meremoti, Eliyasibu, 37 Mataniya, Matenai ndi Yaasu. 38 Pa ana a Binui panali Simeyi, 39 Selemiya, Natani, Adaya, 40 Makinadebai, Sasai, Sarayi, 41 Azareli, Selemiya, Semariya, 42 Salumu, Amariya ndi Yosefe. 43 Pa ana a Nebo panali Yeyeli, Matitiya, Zabadi, Zebina, Yadai, Yoweli ndi Benaya. 44 Onsewa anatenga akazi achilendo+ ndipo akaziwo ndi ana awo anawatumiza kwawo.+

Mabaibulo ena amati, “ndipo amakhala ku Yerusalemu.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “anawalimbitsa manja.”

Nʼkutheka kuti akunena za “Zerubabele” yemwe watchulidwa pa Eza 2:2 ndi 3:8.

Nʼkutheka kuti chinali chigawo cha ku Babulo kapena cha ku Yuda.

Nʼkutheka kuti akunena za “Yoswa” yemwe akutchulidwa pa Hag 1:1 ndi Zek 3:1.

Kapena kuti, “Anetini.” Mʼchilankhulo choyambirira, “Operekedwa.”

Kapena kuti, “Anetini.” Mʼchilankhulo choyambirira, “Operekedwa.”

Kapena kuti, “anawachotsa pa udindo wokhala ansembe chifukwa anali odetsedwa.”

Kapena kuti, “Tirisata.” Dzinali ndi la Chiperisiya la bwanamkubwa wachigawo.

Ena amati “mahosi.”

“Nyulu” ndi nyama yooneka ngati hatchi.

“Dalakima” imeneyi inali yofanana ndi ndalama yagolide ya ku Perisiya yotchedwa dariki, yomwe inkalemera magalamu 8.4. Koma si yofanana ndi dalakima yomwe imatchulidwa mʼMalemba a Chigiriki. Onani Zakumapeto B14.

“Mina” yotchulidwa mʼMalemba a Chiheberi inkalemera magalamu 570. Onani Zakumapeto B14.

Kapena kuti, “Anetini.” Mʼchilankhulo choyambirira, “Operekedwa.”

Akutchulidwa kuti Hodaviya pa Eza 2:40 ndipo pa Ne 7:43 akutchedwa Hodeva.

Mʼchilankhulo choyambirira, “timafunafuna.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “kufooketsa manja.”

Kapena kuti, “anailemba mʼChiaramu nʼkuimasulira.”

Mavesi a Eza 4:8 mpaka 6:18 analembedwa mʼChiaramu.

Kapena kuti, “chakumtsinje wa Firate.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “timadya mchere wa kunyumba yachifumu.”

Mabaibulo ena amati, “yamasuliridwa nʼkuwerengedwa.”

Kapena kuti, “chakumtsinje wa Firate.”

Kapena kuti, “kumaliza khoma lamatabwa.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Maso a Mulungu anali pa.”

Kapena kuti, “kumaliza khoma lamatabwa.”

Nʼkutheka kuti ndi Zerubabele wotchulidwa pa Eza 2:2; 3:8.

Pafupifupi mamita 26.7. Onani Zakumapeto B14.

Kapena kuti, “bwanamkubwa wa chakumtsinje wa Firate.”

Kapena kuti, “mtanda wa nyumba.”

Kapena kuti, “dzala; mulu wa ndowe.”

Onani Zakumapeto B15.

Mʼchilankhulo choyambirira, “afunefune.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “nʼkulimbitsa manja awo.”

Kutanthauza “Thandizo.”

Kapena kuti, “mlembi.”

Kapena kuti, “Iye anali katswiri wokopera.”

Kapena kuti, “Anetini.” Mʼchilankhulo choyambirira, “Operekedwa.”

Kapena kuti, “anatsimikiza mumtima mwake.”

Kapena kuti, “mlembi.”

Kapena kuti, “katswiri wokopera.”

Mavesi a Eza 7:12 mpaka 7:26 analembedwa mʼChiaramu.

Kapena kuti, “mlembi”

Mʼchilankhulo choyambirira, “chimene chili mʼmanja mwako.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “upeze.”

Kapena kuti, “amene ali chakumtsinje wa Firate.”

Kapena kuti, “mlembi.”

Talente imodzi inali yofanana ndi makilogalamu 34.2. Onani Zakumapeto B14.

Muyezo wa kori unali wokwana malita 220. Onani Zakumapeto B14.

Mtsuko umodzi unkakwana malita 22. Onani Zakumapeto B14.

Kapena kuti, “Anetini.” Mʼchilankhulo choyambirira, “Operekedwa.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Mogwirizana ndi nzeru za Mulungu zimene zili mʼmanja mwako.”

Kapena kuti, “ndinadzilimbitsa.”

Kapena kuti, “Anetini.” Mʼchilankhulo choyambirira, “Operekedwa.”

Kapena kuti, “Anetini.” Mʼchilankhulo choyambirira, “Operekedwa.”

Talente imodzi inali yofanana ndi makilogalamu 34.2. Onani Zakumapeto B14.

Dariki ndi ndalama yagolide ya Chiperisiya. Onani Zakumapeto B14.

Limeneli ndi dzina laudindo la “anthu oteteza ufumu.” Palembali akutanthauza abwanamkubwa a mʼzigawo za ufumu wa Perisiya.

Kapena kuti, “abwanamkubwa a chakumtsinje wa Firate.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “chikhomo.”

Kapena kuti, “mumpanda wachitetezo.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena