Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • nwt Song of Solomon 1:1-8:14
  • Nyimbo ya Solomo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Nyimbo ya Solomo
  • Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Nyimbo ya Solomo

NYIMBO YA SOLOMO

1 Nyimbo yoposa nyimbo zonse, nyimbo ya Solomo:+

 2 “Undikise ndi milomo yako,

Chifukwa chikondi chimene umandisonyeza chimaposa vinyo.+

 3 Kununkhira kwa mafuta ako ndi kosangalatsa.+

Dzina lako lili ngati mafuta onunkhira amene athiridwa pamutu.+

Nʼchifukwa chake atsikana amakukonda.

 4 Nditenge, tiye tithawe.

Chifukwatu mfumu yandipititsa mʼzipinda zake zamkati.

Tiye tikondwere komanso kusangalalira limodzi.

Tiye titamande* chikondi chimene umandisonyeza kuposa kutamanda vinyo.

Mpake kuti atsikana amakukonda.

 5 Inu ana aakazi a ku Yerusalemu, ine ndine wakuda koma wokongola,

Ngati matenti a ku Kedara+ komanso nsalu za matenti+ a Solomo.

 6 Musandiyangʼanitsitse chifukwa chakuti ndada,

Ndi dzuwatu landidetsali.

Ana aamuna a mayi anga anandikwiyira.

Choncho anandiika kuti ndiziyangʼanira minda ya mpesa

Moti sindinathe kusamalira munda wanga wa mpesa.

 7 Tandiuze, iwe amene ndimakukonda kwambiri,

Ndiuze kumene umakadyetsera ziweto zako,+

Kumene umakagonetsa ziweto masana.

Kodi ndikhalirenji ngati mkazi amene wafunda nsalu kumutu*

Pakati pa magulu a ziweto za anzako?”

 8 “Ngati iweyo sukudziwa, iwe mkazi wokongola kwambiri kuposa akazi onse,

Tsatira mapazi a ziweto

Ndipo ukadyetse mbuzi zako zingʼonozingʼono pafupi ndi matenti a abusa.”

 9 “Iwe wokondedwa wanga, kwa ine uli ngati hatchi yaikazi yapamagaleta a Farao.+

10 Masaya ako amaoneka bwino ukavala zodzikongoletsera,*

Ndipo khosi lako limaoneka bwino ukavala mikanda.

11 Ife tikupangira zokongoletsa* zagolide

Zokhala ndi mikanda yasiliva.”

12 “Pamene mfumu yakhala patebulo lake lozungulira,

Mafuta anga onunkhira*+ akutulutsa kafungo kosangalatsa.

13 Wachikondi wanga ali ngati kathumba konunkhira ka mule* kwa ine.+

Iye amakhala pakati pa mabere anga usiku wonse.

14 Kwa ine, wachikondi wanga ali ngati maluwa a hena+

Mʼminda ya mpesa ya ku Eni-gedi.”+

15 “Ndiwe wokongola wokondedwa wanga.

Ndiwe chiphadzuwa. Maso ako ali ngati maso a njiwa.”+

16 “Iwenso ndiwe wooneka bwino,* wachikondi wanga komanso ndiwe wosangalatsa.+

Bedi lathu ndi lamasamba ofewa.

17 Nyumba yathu* inamangidwa ndi mitengo ya mkungudza,

Ndipo kudenga kwake kuli mitengo ya junipa.”*

2 “Ine ndine duwa wamba lamʼchigwa chamʼmphepete mwa nyanja,

Ndine duwa chabe lamʼchigwa.”+

 2 “Mofanana ndi duwa limene lili pakati pa minga,

Ndi mmene alili wokondedwa wanga pakati pa ana aakazi.”

 3 “Mofanana ndi mtengo wa maapozi pakati pa mitengo yamʼnkhalango,

Ndi mmene alili wachikondi wanga pakati pa ana aamuna.

Ndikulakalaka kwambiri nditakhala pansi pamthunzi wa wokondedwa wanga.

Ndipo chipatso chake ndi chotsekemera.

 4 Iye anandipititsa kunyumba ya phwando,*

Ndipo chikondi chake kwa ine chinali ngati mbendera yozikidwa pambali panga.

 5 Ndipatseni mphesa zouma zoumba pamodzi+ kuti zinditsitsimule.

Ndipatseni maapozi kuti ndipeze mphamvu,

Chifukwa chikondi chikundidwalitsa.

 6 Dzanja lake lamanzere lili pansi pa mutu wanga,

Ndipo dzanja lake lamanja landikumbatira.+

 7 Ndakulumbiritsani inu ana aakazi a ku Yerusalemu,

Pali insa+ ndiponso pali mphoyo zakutchire kuti:

Musayese kudzutsa chikondi mwa ine nthawi yake isanakwane.+

 8 Ndikumva wachikondi wanga akubwera.

Taonani! Uyo akubwera apoyo,

Akukwera mapiri ndipo akudumpha zitunda.

 9 Wachikondi wanga ali ngati insa komanso mphoyo yaingʼono.+

Taonani! Iye waima kuseri kwa khoma la nyumba yathu.

Akuyangʼana mʼmawindo,

Akusuzumira pazotchingira mʼmawindo.

10 Wachikondi wanga wandiuza kuti:

‘Nyamuka wokondedwa wanga,

Ndiwe wokongola kwa ine, tiye tizipita.

11 Taona! Nyengo yamvula yadutsa.

Mvula yatha ndipo yapita.

12 Maluwa ayamba kuoneka mʼdziko,+

Nthawi yodulira mpesa yakwana,+

Ndipo mʼdziko lathu mukumveka kuimba kwa njiwa.+

13 Nkhuyu zoyambirira+ zapsa mumtengo wa mkuyu.

Mpesa wachita maluwa ndipo ukununkhira.

Nyamuka bwera kuno,

Wokondedwa wanga wokongola, tiye tizipita.

14 Iwe njiwa yanga, amene uli mʼmalo obisika apathanthwe,+

Amene uli mʼmingʼalu yamʼmalo otsetsereka,

Ndikufuna ndikuone komanso kumva mawu ako,+

Chifukwa mawu ako ndi osangalatsa ndipo iweyo ndiwe wokongola.’”+

15 “Tigwirireni nkhandwe,

Nkhandwe zingʼonozingʼono zimene zikuwononga minda ya mpesa,

Chifukwa minda yathu ya mpesa yachita maluwa.”

16 “Wachikondi wanga ndi wanga, ndipo ine ndine wake.+

Iye akudyetsa ziweto msipu+ umene uli pakati pa maluwa.+

17 Mpaka kunja kutayamba kuwomba kamphepo kayaziyazi ndiponso mpaka mithunzi itachoka,

Bwerera mwamsanga iwe wachikondi wanga,

Kwera mapiri amene akutilekanitsa,* ngati insa+ komanso ngati mphoyo yaingʼono.”+

3 “Ndili pabedi panga usiku,

Ndinaganizira za munthu amene ndimamukonda.+

Ndinamufunafuna koma sindinamupeze.+

 2 Choncho ndinati: ‘Ndidzuka nʼkukazungulira mumzinda,

Mʼmisewu ndi mʼmabwalo amumzinda,

Kuti ndikafunefune munthu amene ndimamukonda.’

Ndinamufunafuna koma sindinamupeze.

 3 Alonda amene ankazungulira mumzindawo anandipeza.+

Ndipo ine ndinawafunsa kuti: ‘Kodi mwamuonako munthu amene ndimamukonda?’

 4 Nditangowapitirira pangʼono,

ndinamʼpeza munthu amene ndimamukonda.

Ndinamugwira ndipo sindinafune kumʼsiya

Mpaka nditamubweretsa mʼnyumba ya mayi anga,+

Mʼchipinda chamkati cha mayi amene anali ndi pakati kuti ine ndibadwe.

 5 Ndakulumbiritsani inu ana aakazi a ku Yerusalemu,

Pali insa ndiponso pali mphoyo zakutchire kuti:

Musayese kudzutsa chikondi mwa ine nthawi yake isanakwane.”+

 6 “Kodi chinthu chikuchokera kuchipululuchi nʼchiyani, chooneka ngati utsi wokwera mʼmwamba,

Chonunkhira mafuta a mule ndi lubani,*

Komanso ndi zonunkhira zonse za ufa za munthu wamalonda?”+

 7 “Taonani! Ndi bedi la Solomo.

Lazunguliridwa ndi amuna 60 amphamvu,

Ochokera mwa amuna amphamvu a mu Isiraeli,+

 8 Onsewo atenga malupanga,

Ndipo onse ndi ophunzitsidwa nkhondo,

Aliyense wamangirira lupanga lake mʼchiuno

Kuti adziteteze ku zinthu zoopsa za usiku.”

 9 “Ndi bedi* lachifumu la Mfumu Solomo

Limene anapanga yekha ndi mitengo ya ku Lebanoni.+

10 Zipilala zake ndi zasiliva,

Motsamira mwake ndi mwagolide.

Chokhalira chake ndi chopangidwa ndi ubweya wa nkhosa wapepo.

Mkati mwake, ana aakazi a ku Yerusalemu

Anakongoletsamo posonyeza chikondi.”

11 “Tulukani, inu ana aakazi a Ziyoni,

Pitani mukaone Mfumu Solomo

Itavala nkhata yamaluwa, imene mayi ake+ anailukira

Kuti ivale pa tsiku la ukwati wake,

Pa tsiku limene mtima wa mfumuyo unasangalala.”

4 “Ndiwe wokongola wokondedwa wanga.

Ndiwe chiphadzuwa.

Maso ako ali ngati maso a njiwa munsalu yako yophimba kumutuyo.

Tsitsi lako lili ngati gulu la mbuzi

Zimene zikuthamanga potsika mapiri a ku Giliyadi.+

 2 Mano ako ali ngati gulu la nkhosa zomwe angozimeta kumene,

Zimene zikuchokera kosambitsidwa,

Zonse zabereka mapasa,

Ndipo palibe imene ana ake afa.

 3 Milomo yako ili ngati chingwe chofiira kwambiri,

Ndipo ukamalankhula umasangalatsa.

Masaya ako munsalu yako yophimba kumutuyo

Ali ngati khangaza* logamphula pakati.

 4 Khosi lako+ lili ngati nsanja ya Davide,+

Yomangidwa ndi miyala yokhala mʼmizeremizere,

Pamene akolekapo zishango 1,000,

Zishango zonse zozungulira za amuna amphamvu.+

 5 Mabere ako awiri ali ngati ana awiri a insa

Ngati ana amapasa a insa,+

Amene akudya msipu pakati pa maluwa.”

 6 “Mpaka kunja kutayamba kuwomba kamphepo kayaziyazi ndiponso mpaka mithunzi itachoka,

Ndipita kuphiri la mule

Ndiponso kuzitunda za lubani.”+

 7 “Ndiwe wokongola paliponse, wokondedwa wanga,+

Ndipo ulibe chilema chilichonse.

 8 Tiye tichokere limodzi ku Lebanoni, iwe mkwatibwi wanga,

Tiye tichokere limodzi ku Lebanoni.+

Utsetsereke kuchokera pamwamba pa phiri la Amana,*

Kuchokera pamwamba pa phiri la Seniri, kapena kuti pamwamba pa phiri la Herimoni.+

Utsetsereke kuchokera mʼmapanga a mikango, ndiponso kuchokera kumapiri a akambuku.

 9 Watenga mtima wanga,+ iwe mchemwali wanga, mkwatibwi wanga,

Watenga mtima wanga utangondiyangʼana kamodzi kokha,

Ndiponso ndi mkanda wa mʼkhosi mwako.

10 Chikondi chimene umandisonyeza nʼchokoma,+ iwe mchemwali wanga, mkwatibwi wanga.

Chikondi chimene umandisonyeza nʼchabwino kuposa vinyo,+

Ndipo kununkhira kwa mafuta ako odzola nʼkoposa zonunkhira zamitundu yonse.+

11 Milomo yako imakha uchi wapachisa,+ iwe mkwatibwi wanga.

Uchi ndi mkaka zili kuseri kwa lilime lako,+

Ndipo kafungo konunkhira ka zovala zako kakumveka ngati kafungo konunkhira ka ku Lebanoni.

12 Mchemwali wanga, mkwatibwi wanga, ali ngati munda umene watsekedwa.

Iye ali ngati munda umene watsekedwa, ndiponso ngati kasupe amene watsekedwa.

13 Uli ngati munda* wa mitengo imene nthambi zake zili ndi makangaza ambiri

Umene uli ndi zipatso zabwino kwambiri, maluwa a hena ndi mitengo ya nado,

14 Nado,+ maluwa a safironi, mabango onunkhira,+ sinamoni,+

Komanso mitengo yosiyanasiyana ya lubani, mule, aloye,+

Ndi zonunkhira zonse zabwino kwambiri.+

15 Uli ngati kasupe wamʼmunda, chitsime chamadzi abwino,

Ndiponso timitsinje tochokera ku Lebanoni.+

16 Dzuka, iwe mphepo yakumpoto.

Bwera, iwe mphepo yakumʼmwera.

Womba pamunda wanga.

Kununkhira kwake kufalikire.”

“Wachikondi wanga alowe mʼmunda wake

Kuti adzadye zipatso zake zabwino kwambiri.”

5 “Ndalowa mʼmunda mwanga,+

Iwe mchemwali wanga, mkwatibwi wanga.

Ndathyola mule wanga komanso zonunkhiritsa zanga.+

Ndadya chisa changa cha uchi ndiponso uchi wanga.

Ndamwa vinyo wanga ndi mkaka wanga.”+

“Idyani, inu anthu okondana!

Imwani ndipo muledzere ndi chikondi chimene mukusonyezana.”+

 2 “Panopa ndili mʼtulo koma mtima wanga uli maso.+

Ndikumva wachikondi wanga akugogoda.”

“Nditsegulire iwe mchemwali wanga, wokondedwa wanga,

Njiwa yanga, iwe wopanda chilema.

Chifukwa mutu wanga wanyowa ndi mame,

Tsitsi langa lopotanapotana, lanyowa ndi chinyezi cha usiku.”+

 3 “‘Ndavula mkanjo wanga.

Kodi ndiuvalenso?

Ndatsuka mapazi anga.

Kodi ndiwadetsenso?’

 4 Wachikondi wanga atachotsa dzanja lake pabowo la chitseko,

Mtima wanga unayamba kugunda chifukwa ndinkafunitsitsa kumuona.

 5 Ndinadzuka kuti ndimutsegulire wachikondi wanga.

Manja anga akuyenderera mule,

Ndiponso zala zanga zikuyenderera mafuta a mule,

Mpaka pahandulo ya loko wachitseko.

 6 Ndinamʼtsegulira wachikondi wanga,

Koma wachikondi wangayo anali atachokapo, atapita.

Ndinadandaula kwambiri atachoka.

Ndinamufunafuna koma sindinamupeze.+

Ndinamuitana koma sanandiyankhe.

 7 Alonda amene ankazungulira mumzinda anandipeza.

Anandimenya ndipo anandivulaza.

Alonda apamipanda anandilanda chofunda changa.*

 8 Ndakulumbiritsani inu ana aakazi a ku Yerusalemu kuti:

Mukamʼpeza wachikondi wanga,

Mumuuze kuti ine chikondi chikundidwalitsa.”

 9 “Kodi wachikondi wakoyo akuposa bwanji achikondi ena onse,

Iwe mkazi wokongola kwambiri kuposa akazi onse?

Kodi wachikondi wakoyo akuposa bwanji achikondi ena onse,

Kuti utilumbiritse lumbiro limeneli?”

10 “Wachikondi wanga ndi wokongola ndipo khungu lake ndi lofiira.

Pa amuna 10,000, iye ndi wooneka bwino kwambiri.

11 Mutu wake ndi wokongola ngati golide, golide wabwino kwambiri.

Tsitsi lake lopotanapotana lili ngati nthambi za kanjedza* zimene zikugwedera,

Ndipo ndi lakuda ngati khwangwala.

12 Maso ake ali ngati njiwa zimene zili pafupi ndi mitsinje yamadzi,

Zimene zikusamba mumkaka,

Zitakhala pafupi ndi damu lodzaza madzi.*

13 Masaya ake ali ngati bedi la maluwa onunkhira,+

Ndiponso ngati munda wa zitsamba zonunkhira umene uli pamalo okwera.

Milomo yake ili ngati maluwa amene akuchucha mafuta a mule.+

14 Zala zake zonenepa bwino ndi zagolide, ndipo zikhadabo zake ndi zakulusolito.

Mimba yake ndi yopangidwa ndi minyanga ya njovu yokutidwa ndi miyala ya safiro.

15 Miyendo yake ili ngati zipilala zamiyala ya mabo zozikidwa pazitsulo zagolide wabwino kwambiri.

Iye ndi wokongola ngati dziko la Lebanoni ndipo ndi wamtali mofanana ndi mitengo ya mkungudza.+

16 Mʼkamwa mwake ndi mokoma kwambiri

Ndipo chilichonse mwa iye nʼchosiririka.+

Ameneyu ndi wachikondi wanga, ameneyu ndi wokondedwa wanga, inu ana aakazi a ku Yerusalemu.”

6 “Kodi wachikondi wako wapita kuti,

Iwe mkazi wokongola kwambiri kuposa akazi onse?

Kodi wachikondi wako wadzera njira iti?

Tiye tikuthandize kumufunafuna.”

 2 “Wachikondi wanga wapita kumunda wake,

Kumabedi amʼmunda a mbewu zonunkhira,

Kuti akadyetse ziweto kuminda,

Ndiponso kuti akathyole maluwa.+

 3 Wachikondi wanga, ine ndi wake

Ndipo iye ndi wanga.+

Iye akudyetsera ziweto msipu umene uli pakati pa maluwa.”+

 4 “Wokondedwa wangawe,+ ndiwe wokongola ngati Tiriza,*+

Ndiwe wooneka bwino ngati Yerusalemu,+

Ndipo ndiwe wogometsa ngati magulu a asilikali amene azungulira mbendera.+

 5 Yangʼana kumbali kuti maso ako+ asandiyangʼanitsitse,

Chifukwa akundichititsa mantha.

Tsitsi lako lili ngati gulu la mbuzi

Zimene zikuthamanga potsika mapiri a ku Giliyadi.+

 6 Mano ako ali ngati gulu la nkhosa

Zimene zikuchokera kosambitsidwa,

Zonse zabereka mapasa,

Ndipo palibe imene ana ake afa.

 7 Masaya ako munsalu yako yophimba kumutuyo

Ali ngati khangaza* logamphula pakati.

 8 Ngakhale patakhala mafumukazi 60

Komanso adzakazi* 80

Ndi atsikana osawerengeka,+

 9 Koma mmodzi yekha ndi amene ali njiwa yanga,+ wopanda chilema.

Iye ndi mwana wapadera kwambiri kwa mayi ake.

Ndi mwana amene amakondedwa ndi* mayi amene anamubereka.

Ana aakazi akamuona, amamunena kuti ndi wosangalala.

Mafumukazi ndi adzakazi amamutamanda.

10 ‘Kodi mkazi amene akuwala* ngati mʼbandakuchayu ndi ndani,

Amene ndi wokongola ngati mwezi wathunthu,

Wosadetsedwa ngati kuwala kwa dzuwa,

Wogometsa ngati magulu a asilikali amene azungulira mbendera?’”+

11 “Ine ndinapita kumunda wa mitengo ya zipatso zokhala ndi mtedza,+

Kuti ndikaone ngati yaphuka masamba atsopano mʼchigwa,*

Kuti ndikaone ngati mitengo ya mpesa yaphukira,

Ndiponso ngati mitengo ya makangaza yachita maluwa.

12 Mosazindikira,

Chifukwa cholakalaka kuona zinthu zimenezi, ndinakafika

Kumene kunali magaleta a anthu olemekezeka* a mtundu wanga.”

13 “Bwerera, bwerera iwe Msulami!

Bwerera, bwerera

Kuti tione kukongola kwako!”

“Nʼchifukwa chiyani mukuyangʼanitsitsa Msulami?”+

“Iye ali ngati gule wa magulu awiri a anthu.”*

7 “Mapazi ako akukongola kwambiri munsapato zako,

Iwe mwana wamkazi wolemekezeka.

Ntchafu zako nʼzoumbidwa bwino ngati zinthu zodzikongoletsera,

Ntchito ya manja a munthu waluso.

 2 Mchombo wako uli ngati mbale yolowa.

Vinyo wosakaniza bwino asasowepo.

Mimba yako ili ngati mulu wa tirigu,

Wozunguliridwa ndi maluwa.

 3 Mabere ako awiri ali ngati ana awiri a insa,

Ana amapasa a insa.+

 4 Khosi lako+ lili ngati nsanja ya mnyanga wa njovu.+

Maso ako+ ali ngati madamu a madzi a ku Hesiboni,+

Amene ali pafupi ndi geti la Bati-rabimu.

Mphuno yako ili ngati nsanja ya ku Lebanoni,

Imene inayangʼana cha ku Damasiko.

 5 Mutu wako ndi wokongola ngati phiri la Karimeli,+

Ndipo tsitsi lako lopotanapotana+ lili ngati ubweya wa nkhosa wapepo.+

Mfumu yakopeka* ndi tsitsi lako lalitali lokongolalo.

 6 Ndiwe wokongola kwambiri mtsikana iwe ndipo ndiwe wosangalatsa,

Kuposa zinthu zina zonse zimene zimasangalatsa mtima wa munthu.

 7 Ndiwe wamtali ngati mtengo wa kanjedza,

Ndipo mabere ako ali ngati zipatso zake.+

 8 Ine ndinanena kuti, ‘Ndikwera mtengo wa kanjedza

Kuti ndikathyole nthambi zake zokhala ndi zipatso.’

Mabere ako akhale ngati phava la zipatso za mpesa,

Ndipo mpweya wamʼkamwa mwako ununkhire ngati maapozi,

 9 Ndipo mʼkamwa mwako mununkhire ngati vinyo wabwino kwambiri.”

“Adutse mwamyaa kukhosi kwa wokondedwa wanga,

Ngati vinyo amene amadutsa mwamyaa pakamwa nʼkuyambitsa tulo kwa amuna.

10 Wachikondi wangayo, ine ndine wakewake,+

Ndipo iye amalakalaka ineyo.

11 Bwera wachikondi wanga,

Tiye tipite kumunda.

Tiye tikakhale pakati pa maluwa a hena.+

12 Tiye tilawirire mʼmamawa tipite kuminda ya mpesa.

Tikaone ngati mitengo ya mpesa yaphukira,

Ngati maluwa amasula+

Ngati mitengo ya makangaza yachita maluwa.+

Kumeneko ndikakusonyeza chikondi changa.+

13 Zipatso za mandereki*+ zikununkhira,

Pamakomo olowera kunyumba zathu pali zipatso zosiyanasiyana zokoma kwambiri.+

Ndakusungira zipatso zatsopano ndi zakale zomwe,

Iwe wachikondi wanga.”

8 “Ndikulakalaka ukanakhala mchimwene wanga,

Amene anayamwa mabere a mayi anga.

Ndikanakupeza panja, ndikanakukisa,+

Ndipo palibe amene akanandinyoza.

 2 Bwenzi nditakutsogolera.

Ndikanakulowetsa mʼnyumba mwa mayi anga,+

Amene ankandiphunzitsa.

Ndikanakupatsa vinyo wothira zonunkhiritsa kuti umwe,

Komanso madzi a zipatso za makangaza zongofinya kumene.

 3 Dzanja lake lamanzere likanakhala pansi pa mutu wanga,

Ndipo dzanja lake lamanja likanandikumbatira.+

 4 Ndakulumbiritsani inu ana aakazi a ku Yerusalemu kuti:

Musayese kudzutsa chikondi mwa ine nthawi yake isanakwane.”+

 5 “Kodi ndi ndani amene akuchokera kuchipululuyu,

Atakoleka dzanja lake mʼkhosi mwa wachikondi wake?”

“Ine ndinakudzutsa pansi pa mtengo wa maapozi.

Pamenepo mʼpamene mayi ako anamva zowawa pokubereka.

Mayi amene anakubereka anamva zowawa ali pamenepo.

 6 Undiike pamtima pako ngati chidindo,

Ndiponso undiike ngati chidindo padzanja lako,

Chifukwa mofanana ndi Manda,* chikondi sichigonja,+

Ndipo chimafuna kudzipereka ndi mtima wonse.

Chikondi chimenechi chili ngati malawi a moto. Chikondicho ndi lawi la Ya.*+

 7 Madzi osefukira sangazimitse chikondi,+

Ndipo mitsinje singachikokolole.+

Ngati munthu atapereka chuma chonse chamʼnyumba mwake kusinthanitsa ndi chikondi,

Anthu anganyoze zinthuzo.”*

 8 “Tili ndi mchemwali wathu wamngʼono+

Ndipo alibe mabere.

Kodi tidzamuchitire chiyani mchemwali wathuyu

Pa tsiku limene adzafunsiridwe ukwati?”

 9 “Akakhala khoma,

Timʼmangira kampanda kasiliva pamwamba pake,

Koma akakhala chitseko,

Timʼkhomerera ndi thabwa la mkungudza.”

10 “Ine ndine khoma,

Ndipo mabere anga ali ngati nsanja.

Choncho mʼmaso mwa wokondedwa wanga ndakhala

Ngati mkazi amene wapeza mtendere.

11 Solomo anali ndi munda wa mpesa+ ku Baala-hamoni.

Munda wa mpesawo anaupereka kwa anthu oti aziusamalira.

Ndipo munthu aliyense ankabweretsa ndalama zasiliva zokwana 1,000 zolipirira zipatso za mundawo.

12 Ndili ndi munda wanga wa mpesa umene ndingathe kuchita nawo chilichonse chimene ndikufuna.

Ndalama 1,000 zasilivazo ndi zanu inu a Solomo,

Ndipo ndalama zasiliva 200 ndi za anthu amene amasamalira zipatso za mundawo.”

13 “Iwe amene umakhala mʼminda,+

Anzanga akufuna amve mawu ako.

Inenso ndikufuna ndimve mawu ako.”+

14 “Fulumira wachikondi wanga,

Thamanga ngati insa+

Kapena ngati mphoyo yaingʼono

Pamapiri amaluwa onunkhira.”

Kapena kuti, “Tiye tikambirane za.”

Kapena kuti, “nsalu yovala kumutu polira maliro.”

Mabaibulo ena amati, “Masaya ako ndi okongola ndi nkhata zatsitsi.”

Kapena kuti, “zovala kumutu.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Nado wanga.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Kapena kuti, “ndiwe wokongola.”

Kapena kuti, “Nyumba yathu yabwino kwambiri.”

Mtengo wa junipa ndi wofanana ndi mtengo wa mkungudza.

Mʼchilankhulo choyambirira, “kunyumba ya vinyo.”

Mabaibulo ena amati, “mapiri amipata.” Kapena kuti, “mapiri a Belita.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Limeneli linali bedi lochita kunyamula limene ankanyamulirapo munthu wolemekezeka.

“Khangaza” ndi mtundu wa chipatso. Ena amati chimanga chachizungu.

Kapena kuti, “Anti-Lebanoni.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “paradaiso.”

Kapena kuti, “anandilanda nsalu yanga yofunda kumutu.”

Mabaibulo ena amati, “lili ngati phava la zipatso za kanjedza.”

Mabaibulo ena amati, “Zitakhala mʼmphepete mwa kasupe wa madzi.”

Kapena kuti, “Mzinda Wosangalatsa.”

“Khangaza” ndi mtundu wa chipatso. Ena amati chimanga chachizungu.

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Mʼchilankhulo choyambirira, “Ndi mwana woyera kwa.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “akuyangʼana pansi.”

Kapena kuti, “mʼkhwawa.”

Kapena kuti, “odzipereka.”

Kapena kuti, “gule wa Mahanaimu.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “yatengeka.”

“Mandereki” ndi chitsamba cha mʼgulu la mbatata, chimene chimabereka zipatso.

Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

“Ya” ndi chidule cha dzina lakuti Yehova.

Mabaibulo ena amati, “munthuyo.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena