Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • nwt Ephesians 1:1-6:24
  • Aefeso

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Aefeso
  • Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Aefeso

KALATA YOPITA KWA AEFESO

1 Ine Paulo, mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu, ndine mtumwi wa Khristu Yesu ndipo ndikulembera oyera amene ali ku Efeso,+ amene ndi ophunzira a Khristu Yesu okhulupirika kuti:

2 Mulungu Atate wathu komanso Ambuye Yesu Khristu akupatseni kukoma mtima kwakukulu ndi mtendere.

3 Atamandike Mulungu amene ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, chifukwa watidalitsa ndi dalitso lililonse lauzimu mʼmalo akumwamba mogwirizana ndi Khristu.+ 4 Iye anatisankha kuti tikakhale ogwirizana ndi Khristu dziko lisanakhazikitsidwe nʼcholinga choti tizisonyeza chikondi komanso kuti tikhale oyera ndiponso opanda chilema+ pamaso pa Mulungu. 5 Chifukwa anatisankhiratu+ kuti adzatitenga nʼkukhala ana ake+ kudzera mwa Yesu Khristu, mogwirizana ndi zimene zinamusangalatsa komanso zimene anafuna.+ 6 Anachita zimenezi kuti iye atamandike chifukwa cha kukoma mtima kwakukulu+ kwaulemerero kumene anatisonyeza kudzera mwa mwana wake wokondedwa.+ 7 Kudzera mwa mwana wakeyu, tinamasulidwa ndi dipo* la magazi ake,+ inde, takhululukidwa machimo athu,+ mogwirizana ndi kukoma mtima kwake kwakukulu.

8 Iye anachititsa kuti kukoma mtima kumeneku kukhale kochuluka kwa ife potithandiza kuti tikhale anzeru komanso omvetsa zinthu,* 9 potiululira chinsinsi chake chopatulika+ chokhudza chifuniro chake. Chinsinsicho nʼchogwirizana ndi zimene zimamusangalatsa ndiponso zimene amafuna, 10 zoti akakhazikitse dongosolo lake pa nthawi imene anaikiratu. Dongosolo limenelo ndi kusonkhanitsa zinthu zonse pamodzi kuti zikhale zogwirizana ndi Khristu, zinthu zakumwamba ndi zinthu zapadziko lapansi.+ Inde, zinthu zonse zidzasonkhanitsidwa kwa Khristu, 11 amene chifukwa chogwirizana naye tinasankhidwa kuti tidzalandire cholowa,+ chifukwa anatisankha kale mwa kufuna kwake, iye amene amachita zinthu zonse mogwirizana ndi chifuniro chake. 12 Anachita zimenezo kuti ifeyo amene ndife oyamba kukhala ndi chiyembekezo mwa Khristu titamande Mulungu chifukwa iye ndi wamkulu. 13 Koma inunso munakhala ndi chiyembekezo mwa iye mutamva mawu a choonadi, omwe ndi uthenga wabwino wonena za chipulumutso chanu. Mutakhulupirira, Mulungu anagwiritsa ntchito mzimu woyera umene analonjeza kuti akuikeni chidindo+ ndipo anagwiritsa ntchito Khristu kuti achite zimenezi. 14 Mzimu woyerawo uli ngati chikole chotsimikizira kuti tidzalandira zimene Mulungu watilonjeza.+ Mulungu anachita zimenezi nʼcholinga choti apereke dipo+ kuti anthu ake amasulidwe.+ Zimenezi zidzachititsa kuti atamandidwe komanso kupatsidwa ulemerero.

15 Ndiye chifukwa chake inenso, kuyambira pamene ndinamva za chikhulupiriro chimene muli nacho mwa Ambuye Yesu komanso chikondi chimene mumachisonyeza kwa oyera onse, 16 sindinaleke kuyamika Mulungu chifukwa cha inu. Ndikupitirizabe kukupemphererani, 17 kuti Mulungu wa Ambuye wathu Yesu Khristu, Atate waulemerero, akupatseni mzimu wa nzeru kuti mumvetse zimene Iye akuulula pamene mukuphunzira kuti mumudziwe molondola.+ 18 Mulungu watsegula mitima yanu nʼcholinga choti muone komanso mudziwe chiyembekezo chimene wakupatsani ndiponso zinthu zabwino kwambiri zimene walonjeza kwa oyera,+ 19 ndi kutinso mudziwe kukula kwa mphamvu zake zopambana zimene wazisonyeza kwa okhulupirirafe.+ Mphamvu zake zazikuluzo zikuonekera muntchito zake, 20 pamene anazigwiritsa ntchito poukitsa Khristu kwa akufa nʼkumukhazika kudzanja lake lamanja+ mʼmalo akumwamba. 21 Anamuika pamwamba kuposa boma lililonse, ulamuliro uliwonse, anthu amphamvu onse, ambuye onse, ndi aliyense amene ali ndi dzina laulemu,+ osati mu nthawi* ino yokha, komanso imene ikubwerayo. 22 Mulungu anaikanso zinthu zonse pansi pa mapazi ake,+ ndipo anamuika kuti akhale mutu wa zinthu zonse zimene ndi zokhudzana ndi mpingo+ 23 umene ndi thupi lake+ ndipo ndi wodzaza ndi Khristu, amene amadzaza zinthu zonse mokwanira.

2 Kuwonjezera pamenepo, Mulungu anapangitsa kuti mukhale amoyo ngakhale kuti munali akufa chifukwa cha zolakwa zanu komanso machimo anu.+ 2 Pa nthawi ina munkachita zimenezi mogwirizana ndi nthawi* za mʼdzikoli,+ pomvera wolamulira wa mpweya+ umene umalamulira zochita za anthu. Mpweya umenewu, kapena kuti kaganizidwe+ kameneka, tsopano kakugwira ntchito mwa ana osamvera. 3 Inde, pa nthawi ina pamene tinkakhala pakati pawo, tinkachita zinthu motsatira zilakolako za thupi lathu.+ Tinkachita zofuna za thupi ndi maganizo athu,+ ndipo mwachibadwa tinali ana oyenera kulandira mkwiyo wa Mulungu+ mofanana ndi ena onse. 4 Koma popeza kuti Mulungu ndi wachifundo chochuluka,+ komanso chifukwa cha chikondi chake chachikulu chimene anatisonyeza,+ 5 anapangitsa kuti tikhale amoyo limodzi ndi Khristu, ngakhale kuti tinali akufa chifukwa cha machimo athu,+ ndipotu inu mwapulumutsidwa chifukwa cha kukoma mtima kwakukulu. 6 Kuwonjezera pamenepo, Mulungu anatichititsa kuti tikhale ndi moyo ndipo anatipatsa malo oti tikakhale kumwamba chifukwa anatigwirizanitsa ndi Khristu Yesu.+ 7 Anachita zimenezi kuti mu nthawi* zimene zikubwera, iye adzatisonyeze chuma chopambana cha kukoma mtima kwake kwakukulu. Mulungu adzachita zimenezi potisonyeza chifundo chifukwa ndife ophunzira a Khristu Yesu.

8 Inu amene muli ndi chikhulupiriro, mwapulumutsidwa chifukwa cha kukoma mtima kwakukulu kumeneku.+ Sikuti zimenezi zinatheka chifukwa cha khama lanu, koma ndi mphatso ya Mulungu. 9 Ayi, sikuti zinatheka chifukwa cha ntchito,+ kuti munthu asakhale ndi chifukwa chodzitamandira. 10 Ndife ntchito ya manja a Mulungu. Iye ndi amene anatilenga+ ndipo ndife ogwirizana ndi Khristu Yesu+ kuti tichite ntchito zabwino, zimene Mulungu anakonzeratu kuti tiyendemo.

11 Choncho muzikumbukira kuti nthawi ina, inu amene munali anthu a mitundu ina, anthu odulidwa ankakutchulani kuti anthu osadulidwa. Mdulidwe umenewu umachitika pathupi ndi manja a anthu. 12 Pa nthawi imene ija, Khristu simunkamudziwa, munali otalikirana ndi mtundu wa Isiraeli komanso simunali nawo mʼmapangano a lonjezo.+ Munalibe chiyembekezo ndipo Mulungu simunkamudziwa mʼdzikoli.+ 13 Koma tsopano mogwirizana ndi Khristu Yesu, inu amene pa nthawi ina munali kutali, mwabwera pafupi chifukwa cha magazi a Khristu. 14 Chifukwa iye amene anaphatikiza magulu awiri aja kukhala gulu limodzi+ nʼkugwetsa khoma lomwe linkawalekanitsa limene linali pakati pawo,+ watibweretsera mtendere.+ 15 Ndi thupi lake, anathetsa chinthu choyambitsa chidani, chomwe ndi Chilamulo chimene chinali ndi malamulo komanso malangizo. Anachithetsa kuti magulu awiri omwe ndi ogwirizana ndi iye, akhale munthu mmodzi watsopano+ komanso kuti akhazikitse mtendere. 16 Ndiponso kuti kudzera mwa mtengo wozunzikirapo,*+ agwirizanitse magulu awiri a anthuwo kwa Mulungu ndipo anthuwo akhale thupi limodzi, chifukwa anali atapheratu chidanicho+ kudzera mu imfa yake. 17 Choncho iye anabwera ndipo analengeza uthenga wabwino wa mtendere kwa inu amene munali kutali. Analengezanso za mtendere kwa amene anali pafupi, 18 chifukwa kudzera mwa iye, magulu onse awiriwa angathe kufika kwa Atate mosavuta kudzera mwa mzimu umodzi.

19 Choncho, si inunso anthu osadziwika kapena alendo,+ koma mofanana ndi oyerawo inunso ndinu nzika+ ndipo ndinu a mʼbanja la Mulungu.+ 20 Mwamangidwa pamaziko a atumwi ndi aneneri+ ndipo Khristu Yesu ndi mwala wapakona wa mazikowo.+ 21 Mogwirizana ndi iye, nyumba yonse, popeza ndi yolumikizana bwino,+ ikukula nʼkukhala kachisi woyera wa Yehova.*+ 22 Mogwirizana ndi iye, inunso limodzi ndi anthu ena mukumangidwa pamodzi kuti mukhale malo oti Mulungu akhalemo mwa mzimu.+

3 Choncho, ine Paulo, ndili mʼndende+ chifukwa ndili kumbali ya Khristu Yesu komanso chifukwa chothandiza inu, anthu a mitundu ina— 2 ndithudi, munamva kuti ndinalandira udindo wokuthandizani+ kuti mupindule ndi kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu, 3 ndiponso kuti anandiululira chinsinsi chopatulika, mogwirizana ndi zimene ndinalemba mwachidule mʼmbuyomu. 4 Choncho mukawerenga zimenezi mutha kuzindikira kuti chinsinsi chopatulika+ chonena za Khristu ndikuchimvetsa bwino. 5 Mʼmibadwo yamʼmbuyo, chinsinsi chimenechi sichinaululidwe kwa ana a anthu mmene Mulungu wachiululira panopa kwa atumwi ndi aneneri ake oyera kudzera mwa mzimu.+ 6 Chinsinsi chimenechi nʼchakuti anthu a mitundu ina amene ndi ogwirizana ndi Khristu Yesu, adzalandire cholowa chimene Khristu adzalandire, ndipo adzakhala mbali ya thupi.+ Iwo adzalandiranso zinthu zimene Mulungu watilonjeza chifukwa cha uthenga wabwino. 7 Ndinakhala mtumiki wa zimenezi mogwirizana ndi mphatso yaulere ya kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu, imene ndinapatsidwa pamene anandipatsa mphamvu yake.+

8 Kukoma mtima kwakukulu kumeneku kunaperekedwa kwa ine, munthu wamngʼono pondiyerekeza ndi wamngʼono kwambiri pa oyera onse.+ Ndinapatsidwa kukoma mtima kumeneku+ kuti ndilengeze kwa anthu a mitundu ina uthenga wabwino wonena za chuma chopanda polekezera cha Khristu, 9 ndiponso kuti ndithandize aliyense kuti aone mmene chinsinsi chopatulikacho+ chikuyendetsedwera. Kwa zaka zambiri, Mulungu amene analenga zinthu zonse, wakhala akubisa chinsinsi chimenechi. 10 Zinakhala choncho kuti kudzera mumpingo,+ maboma ndi maulamuliro amene ali mʼmalo akumwamba tsopano adziwe mbali zosiyanasiyana za nzeru za Mulungu.+ 11 Zimenezi nʼzogwirizana ndi cholinga chamuyaya chimene iye anakhala nacho chokhudza Khristu,+ yemwe ndi Yesu Ambuye wathu. 12 Kudzera mwa iye, tili ndi ufulu wa kulankhulawu ndiponso timatha kufika kwa Mulungu mosavuta+ komanso popanda kukayikira chifukwa timakhulupirira Yesu. 13 Choncho ndikukupemphani kuti musafooke poona mavuto amene ndikukumana nawo chifukwa cha inu, popeza mavuto amene ndikukumana nawowa achititsa kuti mulandire ulemerero.+

14 Pa chifukwa chimenechi ndikupinda mawondo anga kwa Atate, 15 amene amapangitsa banja lililonse, kumwamba ndi padziko lapansi, kuti likhale ndi dzina. 16 Ndikupempha kuti Mulungu amene ali ndi ulemerero waukulu, akuloleni kuti munthu wanu wamkati akhale wamphamvu,+ pogwiritsa ntchito mphamvu imene mzimu wake umapereka. 17 Ndikupemphanso kuti mwa chikhulupiriro chanu, mʼmitima yanu mukhale Khristu komanso chikondi.+ Muzike mizu+ ndiponso mukhale okhazikika pamaziko,+ 18 nʼcholinga choti inu limodzi ndi oyera onse muthe kumvetsa bwino mulifupi, mulitali, kukwera ndi kuzama kwa choonadi, 19 ndiponso kuti mudziwe chikondi cha Khristu+ chimene chimaposa kudziwa zinthu, kuti mudzazidwe ndi makhalidwe onse amene Mulungu amapereka.

20 Tsopano kwa iye amene angathe kuchita zazikulu kwambiri kuposa zonse zimene timapempha kapena kuganiza,+ mogwirizana ndi mphamvu yake imene ikugwira ntchito mwa ife,+ 21 kwa iye kukhale ulemerero kudzera mwa mpingo komanso kudzera mwa Khristu Yesu, kumibadwo yonse mpaka muyaya. Ame.

4 Choncho ine, amene ndili mʼndende+ chifukwa cha Ambuye, ndikukuchondererani kuti muzichita zinthu mogwirizana+ ndi kuitana kumene anakuitanani. 2 Nthawi zonse muzichita zinthu modzichepetsa,*+ mofatsa, moleza mtima+ ndiponso muzilolerana chifukwa cha chikondi.+ 3 Muziyesetsa ndi mtima wonse kusunga umodzi umene timaupeza mothandizidwa ndi mzimu woyera, pokhala mwamtendere umene uli ngati chomangira chimene chimatigwirizanitsa.+ 4 Pali thupi limodzi+ ndi mzimu umodzi,+ mogwirizana ndi chiyembekezo chimodzi+ chimene anakuitanirani. 5 Palinso Ambuye mmodzi,+ chikhulupiriro chimodzi, ubatizo umodzi, 6 ndi Mulungu mmodzi amenenso ndi Atate wa anthu onse. Iye ndi wamkulu kuposa wina aliyense, amachita zinthu kudzera mwa tonsefe ndipo mphamvu yake imagwira ntchito mwa onse.

7 Tsopano aliyense wa ife anapatsidwa kukoma mtima kwakukulu mogwirizana ndi mmene Khristu anamuyezera mphatso yaulereyi.+ 8 Chifukwa Malemba amanena kuti: “Atakwera pamalo apamwamba, anatenga anthu ogwidwa ukapolo ndipo anapereka amuna kuti akhale mphatso.”+ 9 Ndiye kodi mawu akuti “atakwera” amatanthauza chiyani? Amatanthauza kuti choyamba anatsika pansi, kutanthauza padziko lapansi. 10 Amene anatsikayo ndi amenenso anakwera+ kukakhala pamwamba kwambiri kuposa kumwamba konse,+ kuti zinthu zonse zikwaniritsidwe.

11 Ndipo pa mphatso zimene anaperekazo, ena anawapereka kuti akhale atumwi,+ ena aneneri,+ ena alaliki*+ ndipo ena abusa ndi aphunzitsi,+ 12 nʼcholinga choti athandize* oyerawo kuti aziyenda mʼnjira yoyenera, kuti azigwira ntchito yotumikira ena komanso kuti amange mpingo umene uli ngati thupi la Khristu,+ 13 mpaka tonse tidzakhale ogwirizana pa zimene timakhulupirira komanso podziwa molondola Mwana wa Mulungu. Zikadzatero, tidzakhala anthu achikulire, amene afika pa msinkhu wa munthu wamkulu+ ngati mmene Khristu analili. 14 Choncho tisakhalenso ana. Tisamatengeketengeke ngati kuti tikukankhidwa ndi mafunde ndiponso tisamatengeke kupita uku ndi uku ndi mphepo iliyonse ya zinthu zachinyengo zimene anthu amaphunzitsa+ popeka mabodza mochenjera. 15 Koma tizilankhula zoona ndiponso kusonyeza chikondi. Tikatero tidzakhala achikulire mʼzinthu zonse ndipo tidzatha kuchita zinthu mogwirizana ndi Khristu, amene ndi mutu.+ 16 Tili ngati thupi,+ ndipo chifukwa cha iye, ziwalo zonse za thupi limeneli ndi zolumikizana bwino ndipo zimathandiza thupilo kuti lizigwira bwino ntchito. Chiwalo chilichonse cha thupili chikamagwira ntchito yake, thupili limakula bwino ndipo tidzapitiriza kukondana.+

17 Choncho ndikunena komanso kuchitira umboni mwa Ambuye, kuti musapitirize kuyenda ngati mmene anthu a mitundu ina amayendera,+ potsatira maganizo awo opanda pake.+ 18 Iwo ali mumdima wa maganizo ndipo ndi otalikirana ndi moyo umene umachokera kwa Mulungu, chifukwa cha umbuli umene uli mwa iwo komanso chifukwa cha kuuma kwa mitima yawo. 19 Popeza iwo sakuthanso kuzindikira makhalidwe abwino, anadzipereka okha ku khalidwe lopanda manyazi*+ kuti achite zonyansa zamtundu uliwonse mwadyera.

20 Koma inu simunaphunzire kuti Khristu ndi wotero. 21 Yesu ankaphunzitsa choonadi, moti ngati munamva zimene ankaphunzitsa ndiponso munaphunzitsidwa ndi iye, ndiye kuti zinthu zimenezo mukuzidziwa bwino. 22 Munaphunzitsidwa kuti muvule umunthu wakale+ umene umagwirizana ndi makhalidwe anu akale, umenenso ukuipitsidwa chifukwa cha zilakolako zachinyengo za umunthuwo.+ 23 Ndipo mupitirize kusintha kuti mukhale atsopano pa kaganizidwe kanu komanso mmene mumaonera zinthu.*+ 24 Ndipo muvale umunthu watsopano+ umene unalengedwa mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu. Mukachita zimenezi mudzatha kuchita zimene zilidi zolungama ndi zokhulupirika.

25 Choncho, popeza tsopano mwataya chinyengo, aliyense wa inu azilankhula zoona kwa mnzake,+ chifukwa ndife ziwalo zolumikizana.+ 26 Ngati mwakwiya, musachimwe.+ Dzuwa lisalowe mudakali okwiya.+ 27 Musamupatse mpata Mdyerekezi.*+ 28 Munthu wakuba asiye kubako, koma azigwira ntchito molimbikira. Azigwira ntchito yabwino ndi manja ake+ kuti azitha kupeza zinthu zimene angathe kugawana ndi munthu wosowa.+ 29 Mawu owola asamatuluke pakamwa panu,+ koma pazituluka mawu abwino okha kuti alimbikitse ena pakafunika kutero, kuti athandize anthu amene akumvetsera.+ 30 Komanso, musamamvetse chisoni mzimu woyera wa Mulungu,+ umene Mulunguyo anaugwiritsa ntchito pokuikani chidindo+ kuti mudzamasulidwe ndi dipo+ pa tsiku lachipulumutso.

31 Chidani chachikulu,+ kupsa mtima, mkwiyo, kulalata, mawu achipongwe+ komanso zinthu zonse zoipa zichotsedwe mwa inu.+ 32 Koma muzikomerana mtima, muzisonyezana chifundo chachikulu+ komanso muzikhululukirana ndi mtima wonse, ngati mmene inunso Mulungu anakukhululukirani ndi mtima wonse kudzera mwa Khristu.+

5 Choncho muzitsanzira Mulungu,+ monga ana ake okondedwa, 2 ndipo pitirizani kusonyeza chikondi+ ngati mmene Khristu anatikondera*+ nʼkudzipereka yekha chifukwa cha ife* ngati chopereka ndiponso ngati nsembe yafungo lokoma kwa Mulungu.+

3 Nkhani zachiwerewere* komanso chonyansa chamtundu uliwonse kapena umbombo zisatchulidwe nʼkomwe pakati panu,+ chifukwa anthu oyera sayenera kuchita zimenezi.+ 4 Musatchule ngakhale nkhani zokhudza khalidwe lochititsa manyazi, nkhani zopusa kapena nthabwala zotukwana+ chifukwa ndi zinthu zosayenera. Mʼmalomwake muziyamika Mulungu.+ 5 Chifukwa mfundo iyi mukuidziwa ndipo mukuimvetsa bwino, kuti munthu wachiwerewere*+ kapena wodetsedwa kapena waumbombo,+ umene ndi kulambira mafano, sadzalowa mu Ufumu wa Khristu ndi wa Mulungu.+

6 Munthu asakupusitseni ndi mawu opanda pake, chifukwa mkwiyo wa Mulungu udzafika pa ana a osamvera, amene akuchita zinthu zimene ndatchulazi. 7 Choncho musamachite zimene iwo amachita.* 8 Chifukwa poyamba munali ngati mdima, koma pano muli ngati kuwala+ popeza ndinu ogwirizana ndi Ambuye.+ Pitirizani kuyenda ngati ana a kuwala. 9 Chifukwa zipatso za kuwala ndi chilichonse chabwino, chilichonse cholungama ndi choona.+ 10 Nthawi zonse muzitsimikizira kuti chovomerezeka+ kwa Ambuye nʼchiti. 11 Ndipo musiye kuchita nawo ntchito zosapindulitsa zamumdima.+ Mʼmalomwake, muzisonyeza poyera kuti ndi zinthu zoipa. 12 Chifukwa zinthu zimene iwo amachita mwachinsinsi ndi zochititsa manyazi ngakhale kuzitchula. 13 Tsopano zinthu zimene zikuululidwa* zimaonekera poyera chifukwa cha kuwala, popeza chilichonse chimene chaonekera chimakhala kuwala. 14 Nʼchifukwa chake pali mawu akuti: “Dzuka, wogona iwe! Uka kwa akufa+ ndipo Khristu adzawala pa iwe.”+

15 Choncho samalani kwambiri kuti mukamayenda, musamayende ngati anthu opanda nzeru koma ngati anthu anzeru. 16 Muzigwiritsa ntchito bwino nthawi yanu*+ chifukwa masikuwa ndi oipa. 17 Pa chifukwa chimenechi, siyani kuchita zinthu ngati anthu opanda nzeru, koma pitirizani kuzindikira chifuniro cha Yehova.*+ 18 Ndiponso musamaledzere ndi vinyo+ chifukwa kuledzera kungachititse kuti muchite zinthu zoipa kwambiri, koma pitirizani kudzazidwa ndi mzimu. 19 Muziimbira limodzi masalimo, nyimbo zotamanda Mulungu ndiponso nyimbo zauzimu.+ Muziimba nyimbo+ zotamanda Yehova* mʼmitima yanu.+ 20 Nthawi zonse muziyamika+ Mulungu, Atate wathu, pa zinthu zonse mʼdzina la Ambuye wathu Yesu Khristu.+

21 Muzigonjerana+ poopa Khristu. 22 Akazi azigonjera amuna awo+ ngati mmene amagonjerera Ambuye, 23 chifukwa mwamuna ndi mutu wa mkazi wake+ mofanana ndi Khristu amene ndi mutu wa mpingo,+ popeza iye ndi mpulumutsi wa thupi* limeneli. 24 Ndipotu, mofanana ndi mmene mpingo umagonjerera Khristu, akazinso azigonjera amuna awo pa chilichonse. 25 Amuna inu, pitirizani kukonda akazi anu+ ngati mmenenso Khristu anakondera mpingo nʼkudzipereka yekha chifukwa cha mpingowo,+ 26 nʼcholinga choti auyeretse pousambitsa mʼmadzi a mawu a Mulungu.+ 27 Anachita zimenezi kuti iyeyo alandire mpingowo uli wokongola ndiponso waulemerero, wopanda banga kapena makwinya kapenanso chilichonse cha zinthu zoterezi,+ koma kuti ukhale woyera ndi wopanda chilema.+

28 Mofanana ndi zimenezi, amuna azikonda akazi awo ngati mmene amakondera matupi awo. Mwamuna amene amakonda mkazi wake amadzikonda yekha, 29 chifukwa palibe munthu amene anadanapo ndi thupi lake, koma amalidyetsa ndi kulikonda, ngati mmene Khristu amachitira ndi mpingo 30 chifukwa ndife ziwalo za thupi lake.+ 31 “Chifukwa cha zimenezi mwamuna adzasiya bambo ake ndi mayi ake nʼkudziphatika kwa* mkazi wake ndipo awiriwo adzakhala thupi limodzi.”+ 32 Chinsinsi chopatulika+ chimenechi nʼchachikulu. Tsopano ndikulankhula za Khristu ndi mpingo.+ 33 Komabe, aliyense wa inu azikonda mkazi wake+ ngati mmene amadzikondera yekha komanso mkazi azilemekeza kwambiri mwamuna wake.+

6 Ana inu, muzimvera makolo anu+ mogwirizana ndi zimene Ambuye amafuna, chifukwa kuchita zimenezi nʼkoyenera. 2 “Muzilemekeza bambo anu ndi mayi anu.”+ Limeneli ndi lamulo loyamba lokhala ndi lonjezo. Lonjezo lake ndi lakuti: 3 “Kuti zinthu zikuyendereni bwino, ndiponso kuti mukhale ndi moyo wautali padziko lapansi.” 4 Inu abambo, musamapsetse mtima ana anu,+ koma pitirizani kuwalera powapatsa malangizo*+ komanso kuwaphunzitsa mogwirizana ndi zimene Yehova* amanena.+

5 Akapolo inu, muzimvera anthu amene ndi ambuye anu.+ Muziwaopa ndi kuwalemekeza kuchokera pansi pa mtima, ngati mmene mumachitira ndi Khristu. 6 Musamachite zimenezi pokhapokha pamene anthu akukuonani pongofuna kuwasangalatsa,*+ koma ngati akapolo a Khristu amene akuchita chifuniro cha Mulungu ndi mtima wonse.+ 7 Muzitumikira ambuye anu modzipereka, ngati mukutumikira Yehova*+ osati anthu, 8 chifukwa mukudziwa kuti pa chabwino chilichonse chimene munthu angachite, Yehova* adzamupatsa mphoto,+ kaya munthuyo ndi kapolo kapena mfulu. 9 Inu ambuye, muzichitiranso akapolo anu chimodzimodzi. Musamawaopseze chifukwa mukudziwa kuti Ambuye wa nonsenu, wa iwowo ndi wa inuyo, ali kumwamba+ ndipo alibe tsankho.

10 Pomaliza ndikuti, pitirizani kupeza mphamvu+ kuchokera kwa Ambuye chifukwa mphamvu zake nʼzazikulu. 11 Valani zida zonse zankhondo+ zochokera kwa Mulungu kuti musagonje polimbana ndi zochita zachinyengo* za Mdyerekezi, 12 chifukwa sitikulimbana+ ndi anthu athupi la magazi ndi nyama, koma tikulimbana ndi ziwanda+ zimene zili kumwamba, zomwe ndi maboma komanso maulamuliro amene akulamulira dziko limene lili mumdimali. 13 Pa chifukwa chimenechi, nyamulani zida zonse zankhondo zochokera kwa Mulungu+ kuti patsiku loipa musadzagonje, ndiponso kuti mutachita zonse bwinobwino, mudzathe kulimba.

14 Choncho khalani olimba, mutamanga kwambiri choonadi mʼchiuno mwanu ngati lamba,+ mutavala chodzitetezera pachifuwa chachilungamo,+ 15 komanso mutavala nsapato kumapazi anu pokonzekera kulengeza uthenga wabwino wamtendere.+ 16 Koposa zonsezi, nyamulani chishango chachikulu chachikhulupiriro,+ chimene mudzathe kuzimitsira mivi yonse yoyaka moto ya woipayo.+ 17 Komanso valani chipewa cha chipulumutso+ ndipo nyamulani lupanga la mzimu, lomwe ndi mawu a Mulungu.+ 18 Pamene mukuchita zimenezi, muzipemphera pa chochitika chilichonse mu mzimu,+ pogwiritsa ntchito pemphero+ ndi pembedzero la mtundu uliwonse. Kuti muchite zimenezi khalani maso ndipo nthawi zonse muzipemphera mopembedzera mʼmalo mwa oyera onse. 19 Muzindipemphereranso ineyo kuti ndikayamba kulankhula ndizipeza mawu oyenerera nʼcholinga choti ndizitha kulankhula molimba mtima ndikamalalikira zokhudza chinsinsi chopatulika cha uthenga wabwino,+ 20 umene ndine kazembe+ wake womangidwa ndi unyolo ndiponso kuti ndilankhule za uthengawo molimba mtima ngati mmene ndikuyenera kuchitira.

21 Tsopano, kuti mudziwenso mmene zinthu zikuyendera pa moyo wanga ndi mmene ine ndilili, Tukiko,+ mʼbale wokondedwa ndiponso mtumiki wokhulupirika wa Ambuye, adzakufotokozerani zonse.+ 22 Ndamutumiza kwa inu ndi cholinga chimenechi, kuti mudziwe za moyo wathu ndiponso kuti atonthoze mitima yanu.

23 Mtendere ndi chikondi ndiponso chikhulupiriro zochokera kwa Mulungu Atate ndi kwa Ambuye Yesu Khristu, zikhale pa abalenu. 24 Kukoma mtima kwakukulu kukhale pa onse amene ali ndi chikondi chenicheni pa Ambuye wathu Yesu Khristu.

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Kapena kuti, “komanso ozindikira.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Onani Zakumapeto A5.

Kapena kuti, “ndi maganizo odzichepetsa.”

Kapena kuti, “olalikira uthenga wabwino.”

Kapena kuti, “aphunzitse.”

MʼChigiriki a·sel′gei·a. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Kapena kuti, “komanso mphamvu yoyendetsa maganizo anu.” Mʼchilankhulo choyambirira, “mzimu wa maganizo anu.”

Kapena kuti, “Musamupatse malo Mdyerekezi.”

Mabaibulo ena amati, “anakukonderani.”

Mabaibulo ena amati, “inu.”

MʼChigiriki por·nei′a. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Kapena kuti, “Choncho musamacheze nawo.”

Kapena kuti, “zikudzudzulidwa.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Muzigula nthawi yoikidwiratu.”

Onani Zakumapeto A5.

Onani Zakumapeto A5.

Kutanthauza mpingo.

Kapena kuti, “nʼkumakhala ndi.”

Mawu amʼchilankhulo choyambirira amene amasuliridwa kuti “malangizo” ali ndi matanthauzo ambiri. Akhoza kutanthauza malangizo, kuphunzitsa, kudzudzula, kulimbikitsa, kulanga kapena uphungu.

Onani Zakumapeto A5.

Mʼchilankhulo choyambirira, “mwachiphamaso pofuna kusangalatsa anthu.”

Onani Zakumapeto A5.

Onani Zakumapeto A5.

Kapena kuti, “ndi ziwembu.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena