2 Samueli
5 Patapita nthawi, mafuko onse a Isiraeli anapita kwa Davide+ ku Heburoni+ ndi kumuuza kuti: “Ife ndife fupa lanu ndi mnofu wanu.+ 2 Kuyambira kale+ pamene Sauli anali mfumu yathu, inuyo munali kutsogolera Isiraeli polowa ndi potuluka.+ Ndipo Yehova anakuuzani kuti, ‘Udzaweta+ anthu anga Aisiraeli ndipo udzakhala mtsogoleri+ wa Isiraeli.’” 3 Choncho akulu onse+ a Isiraeli anabwera kwa mfumu ku Heburoni, ndipo Mfumu Davide anachita nawo pangano+ ku Heburoni pamaso pa Yehova. Kenako iwo anadzoza+ Davide kukhala mfumu ya Isiraeli.+
4 Davide anali ndi zaka 30 pamene anakhala mfumu. Iye analamulira monga mfumu kwa zaka 40.+ 5 Ku Heburoni analamulira monga mfumu ya Yuda zaka 7 ndi miyezi 6.+ Ku Yerusalemu+ analamulira monga mfumu ya Isiraeli yense ndiponso Yuda zaka 33. 6 Patapita nthawi, mfumu ndi anthu ake anapita ku Yerusalemu kukamenyana ndi Ayebusi+ amene anali kukhala kumeneko. Ayebusiwo anayamba kuuza Davide kuti: “Sulowa mumzinda uno, pakuti upitikitsidwa ndi anthu akhungu ndi olumala.”+ Mumtima mwawo iwo anali kunena kuti: “Davide sangalowe mumzinda uno.” 7 Ngakhale zinali choncho, Davide analanda Ziyoni, malo okhala mumpanda wolimba kwambiri,+ umene ndi Mzinda wa Davide.+ 8 Choncho Davide pa tsiku limenelo anati: “Aliyense wofuna kukaukira Ayebusi+ adutse m’ngalande zamadzi+ ndi kukakumana ndi anthu olumala ndi akhungu, anthu amene ine Davide ndimadana nawo kwambiri!” N’chifukwa chake pali mawu onena kuti: “Wakhungu ndi wolumala asalowe m’nyumba.” 9 Davide anayamba kukhala m’malo okhala mumpanda wolimba kwambiri, ndipo anawatcha Mzinda wa Davide. Iye anayamba kumanga malo onsewo kuyambira ku Chimulu cha Dothi*+ mpaka mkati. 10 Chotero ulamuliro wa Davide unakulirakulira,+ ndipo Yehova Mulungu wa makamu+ anali naye.+
11 Ndiyeno Hiramu+ mfumu ya Turo anatumiza amithenga+ kwa Davide. Anatumizanso mitengo ya mkungudza,+ anthu a ntchito zamatabwa ndi a ntchito za miyala yomangira khoma,* ndipo anayamba kumanga nyumba ya Davide.+ 12 Davide anadziwa kuti Yehova wachititsa kuti ufumu wake ukhazikike mu Isiraeli,+ komanso kuti wamukwezera+ ufumu wake chifukwa cha anthu ake Aisiraeli.+
13 Pambuyo pake, Davide anatenganso adzakazi+ ndi akazi+ ena mu Yerusalemu atachoka ku Heburoni, moti anaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi. 14 Ana amene Davide anabereka ku Yerusalemu mayina awo ndi awa: Samuwa,+ Sobabu,+ Natani,+ Solomo,+ 15 Ibara, Elisua,+ Nefegi,+ Yafiya,+ 16 Elisama,+ Eliyada ndi Elifeleti.+
17 Tsopano Afilisiti anamva kuti Davide amudzoza kukhala mfumu ya Isiraeli.+ Choncho Afilisiti onse anabwera kudzafunafuna Davide. Davide atamva zimenezi, anakabisala kumalo ovuta kufikako.+ 18 Afilisitiwo anafika ndi kuyamba kuyendayenda m’chigwa cha Arefai.+ 19 Ndiyeno Davide anafunsira+ kwa Yehova kuti: “Kodi ndipite kukamenyana ndi Afilisitiwa? Kodi muwapereka m’manja mwanga?” Pamenepo Yehova anauza Davide kuti: “Pita, ndipereka ndithu Afilisitiwa m’manja mwako.”+ 20 Choncho Davide anapita ku Baala-perazimu,+ ndipo anapha Afilisiti kumeneko. Atatero anati: “Yehova wayenda patsogolo panga ngati madzi a chigumula ndi kuwononga adani anga.”+ N’chifukwa chake malowo anawatcha Baala-perazimu.*+ 21 Pa nthawiyi, Afilisiti anasiya mafano awo+ kumeneko, choncho Davide ndi anthu ake anawatenga.+
22 Patapita nthawi, Afilisiti aja anabweranso+ ndi kuyamba kuyendayenda m’chigwa cha Arefai.+ 23 Pamenepo Davide anafunsira+ kwa Yehova ndipo anamuyankha kuti: “Ayi usapite. Koma uwazembere kumbuyo kwawo ndi kuwaukira kutsogolo kwa zitsamba za baka.*+ 24 Ndiyeno ukakamva phokoso la kuguba pamwamba pa zitsamba za baka, pamenepo ukachitepo kanthu mwachangu,+ chifukwa pa nthawiyo Yehova adzakhala atatsogola kukapha gulu lankhondo la Afilisiti.”+ 25 Pamenepo Davide anachitadi momwemo, monga mmene Yehova anamulamulira,+ moti anapha+ Afilisiti kuchokera ku Geba*+ mpaka kukafika ku Gezeri.+