YEREMIYA
1 Awa ndi mawu a Yeremiya* mwana wa Hilikiya, mmodzi wa ansembe a ku Anatoti,+ mʼdera la Benjamini. 2 Yeremiya analandira mawu ochokera kwa Yehova mʼmasiku a Yosiya+ mwana wa Amoni,+ mfumu ya Yuda, mʼchaka cha 13 cha ulamuliro wa Yosiya. 3 Yeremiya analandiranso mawuwo mʼmasiku a Yehoyakimu+ mwana wa Yosiya, mfumu ya Yuda mpaka kumapeto kwa chaka cha 11 cha ulamuliro wa Zedekiya+ mwana wa Yosiya, mfumu ya Yuda, komanso mpaka pamene anthu a mu Yerusalemu anatengedwa kupita ku ukapolo mʼmwezi wa 5.+
4 Ndiyeno Yehova anandiuza kuti:
5 “Ndisanakuumbe mʼmimba, ndinkakudziwa,*+
Ndipo usanabadwe,* ndinakusankha* kuti ugwire ntchito yopatulika.+
Ndinakusankha kuti ukhale mneneri ku mitundu ya anthu.”
6 Koma ine ndinati: “Ayi musatero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa!
Ine sinditha kulankhula+ chifukwa ndine mwana.”+
7 Ndiyeno Yehova anandiuza kuti:
“Usanene kuti, ‘Ndine mwana,’
Chifukwa ukuyenera kupita kwa anthu onse kumene ndidzakutume,
Ndipo ukanene zonse zimene ndakulamula.+
8 Usachite mantha ndi maonekedwe awo,+
Chifukwa ‘Ine ndili ndi iwe kuti ndikupulumutse,’+ akutero Yehova.”
9 Kenako Yehova anatambasula dzanja lake nʼkukhudza pakamwa panga.+ Ndiyeno Yehova anandiuza kuti: “Ndaika mawu anga mʼkamwa mwako.+ 10 Taona, lero ndakupatsa mphamvu pa mitundu ya anthu ndi maufumu, kuti uzule ndi kugwetsa, uwononge ndi kupasula, komanso kuti umange ndi kudzala.”+
11 Ndiyeno Yehova anandifunsa kuti: “Ukuona chiyani Yeremiya?” Ine ndinayankha kuti: “Ndikuona nthambi ya mtengo wa amondi.”*
12 Yehova anandiuza kuti: “Waona bwino, chifukwa ndili maso ndipo ndine wokonzeka kukwaniritsa mawu anga.”
13 Yehova anandifunsanso kachiwiri kuti: “Ukuona chiyani?” Ine ndinayankha kuti: “Ndikuona mphika wa kukamwa kwakukulu umene ukuwira* ndipo wafulatira kumpoto koma kukamwa kwake kwaloza kumʼmwera.” 14 Kenako Yehova anandiuza kuti:
“Tsoka lidzachokera kumpoto
Ndipo lidzagwera anthu onse okhala mʼdzikoli.+
15 Yehova wanena kuti, ‘Ndikuitana mafuko onse a maufumu a kumpoto.+
Iwo adzabwera ndipo aliyense adzakhazikitsa mpando wake wachifumu,
Pakhomo la mageti a Yerusalemu.+
Iwo adzaukira mpanda wake wonse
Ndi mizinda yonse ya Yuda.+
16 Ndipo ine ndidzapereka zigamulo zanga pa anthu anga chifukwa cha zoipa zawo zonse,
Chifukwa iwo andisiya+
Ndipo akupereka nsembe zofukiza kwa milungu ina+
Komanso akugwadira ntchito za manja awo.’+
17 “Koma iwe ukonzekere kugwira ntchito,*
Ndipo upite ukawauze zonse zimene ndakulamula.
Usachite nawo mantha,+
Kuti ndisakupangitse kuchita nawo mantha kwambiri.
18 Chifukwa lero ndakupanga kuti ukhale mzinda wokhala ndi mpanda wolimba kwambiri,
Chipilala cha chitsulo ndi makoma akopa* kuti dziko lonseli lisakugonjetse.+
Kuti mafumu a Yuda, akalonga ake,
Ansembe ake ndi anthu amʼdzikoli asakugonjetse.+
19 Iwo adzamenyana nawe ndithu,
Koma sadzakugonjetsa,
Chifukwa Yehova wanena kuti, ‘Ine ndili ndi iwe+ kuti ndikupulumutse.’”
2 Yehova anandiuza kuti: 2 “Pita, ukalengeze kwa anthu a ku Yerusalemu kuti, ‘Yehova wanena kuti:
“Ndikukumbukira bwino mmene unkadziperekera* uli wachinyamata,+
Chikondi chimene unkasonyeza pa nthawi imene ndinakulonjeza kuti ndidzakukwatira,+
Mmene unanditsatirira mʼchipululu,
Mʼdziko losadzalidwa kalikonse.+
3 Isiraeli anali wopatulika kwa Yehova,+ ndipo anali zipatso zoyambirira pa zokolola zake.”’
‘Aliyense wofuna kumumeza akanakhala ndi mlandu.
Tsoka likanamugwera,’ akutero Yehova.”+
4 Tamverani mawu a Yehova, inu a mʼnyumba ya Yakobo
Komanso inu nonse mafuko a mʼnyumba ya Isiraeli.
5 Yehova wanena kuti:
“Kodi makolo anu anandipeza ndi vuto lotani+
Kuti asochere nʼkupita kutali ndi ine,
Nʼkuyamba kutsatira mafano opanda pake,+ iwonso nʼkukhala anthu opanda pake?+
6 Iwo sanafunse kuti, ‘Ali kuti Yehova,
Amene anatitulutsa mʼdziko la Iguputo,+
Amene anatitsogolera mʼchipululu,
Mʼdziko la zipululu+ ndi mayenje,
Mʼdziko lachilala+ ndi lamdima wandiweyani,
Mʼdziko limene simudutsa munthu aliyense
Komanso mmene simukhala anthu?’
7 Kenako ndinakulowetsani mʼdziko la minda ya zipatso,
Kuti mudye zipatso zake ndi zinthu zabwino zamʼdzikolo.+
Koma inu munalowa mʼdziko langa nʼkuliipitsa.
Cholowa changa munachisandutsa chinthu chonyansa.+
8 Ansembe sanafunse kuti, ‘Ali kuti Yehova?’+
Amene ankaphunzitsa Chilamulo sankandidziwa,
Abusa anandipandukira,+
Aneneri ankalosera mʼdzina la Baala,+
Ndipo ankatsatira milungu yopanda phindu.
9 ‘Choncho ndipitiriza kukuimbani mlandu,’+ akutero Yehova,
‘Ndipo ndidzaimbanso mlandu ana a ana anu.’
10 ‘Koma wolokerani kuzilumba za ku Kitimu+ kuti muone.
Tumizani anthu ku Kedara+ ndipo muganizire bwinobwino
Nʼkuona ngati zoterezi zinayamba zachitikapo kumeneko.
11 Kodi pali mtundu uliwonse wa anthu umene unasinthapo milungu yawo nʼkuyamba kulambira milungu imene kulibeko?
Koma anthu anga asinthanitsa ulemerero wanga ndi zinthu zopanda phindu.+
12 Yangʼanitsitsani zimenezi modabwa, inu kumwamba,
Ndipo munjenjemere ndi mantha aakulu kwambiri,’ akutero Yehova,
13 ‘Chifukwa anthu anga achita zinthu ziwiri zoipa:
Iwo andisiya ine kasupe wa madzi amoyo,+
Ndipo akumba* zitsime zawo,
Zitsime zongʼambika zimene sizingasunge madzi.’
14 ‘Kodi Isiraeli ndi mtumiki wanga kapena ndi kapolo wobadwira mʼnyumba mwanga?
Nanga nʼchifukwa chiyani anthu anamugwira nʼkupita naye kudziko lina?
Yachititsa kuti dziko lake likhale chinthu chochititsa mantha.
Mizinda yake aiyatsa moto, moti simukukhalanso munthu aliyense.
16 Anthu a ku Nofi*+ ndi ku Tahapanesi+ anawononga dziko lako.*
17 Kodi mavuto amenewa sunadzibweretsere wekha,
Posiya Yehova Mulungu wako+
Pa nthawi imene ankakutsogolera panjira?
18 Ndiye nʼchifukwa chiyani ukufuna kuyenda mʼnjira ya ku Iguputo+
Kuti ukamwe madzi amumtsinje wa Sihori?*
Nʼchifukwa chiyani ukufuna kuyenda mʼnjira yopita kudziko la Asuri+
Kuti ukamwe madzi amumtsinje wa Firate?
19 Uphunzirepo kanthu pa kuipa kwako,
Ndipo kusakhulupirika kwako kukudzudzule.
Udziwe ndi kuzindikira kuti kusiya Yehova Mulungu wako+
Nʼchinthu choipa komanso chowawa.
Iwe wasonyeza kuti sumandiopa,’+ akutero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Ambuye Wamkulu Koposa.
20 ‘Ine ndinaphwanya goli lako kalekale+
Nʼkudula zingwe zimene anakumangira.
Koma iwe unanena kuti: “Ine sindikutumikirani,”
Ndipo unkagona chagada paphiri lililonse lalitali ndi pansi pa mtengo uliwonse waukulu wa masamba obiriwira+
Nʼkumachita uhule pamenepo.+
21 Ine ndinakudzala ngati mtengo wa mpesa wofiira,+ wabwino kwambiri umene unamera kuchokera ku mbewu yabwino kwambiri.
Ndiye wandisinthira bwanji nʼkukhala mphukira zachabechabe za mtengo wa mpesa wachilendo?’+
22 ‘Ngakhale utasambira soda ndiponso sopo wambiri,
Zolakwa zako ndidzazionabe ngati zinthu zothimbirira,’+ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.
23 Unganene bwanji kuti, ‘Sindinadziipitse.
Sindinatsatire mafano a Baalaʼ?
Ganizira bwinobwino mmene ukuyendera mʼchigwa.
Ganizira zimene wachita.
Uli ngati ngamila yaingʼono yaikazi yothamanga kwambiri,
Imene ikuthamanga kupita uku ndi uku popanda cholinga,
24 Uli ngati bulu wamʼtchire amene anazolowera kukhala mʼchipululu,
Amene amanunkhiza pofunafuna amuna chifukwa cha chilakolako chake champhamvu.
Ndi ndani amene angamubweze nthawi yoti akweredwe ikakwana?
Abulu amphongo amene akumufunafuna sadzavutika kuti amupeze.
Nyengo yoti* akweredwe ikakwana adzamupeza.
25 Samala kuti phazi lako lisakhale lopanda nsapato
Komanso kuti usachite ludzu.
Koma iwe unanena kuti, ‘Zimenezo ayi!+
26 Anthu a mʼnyumba ya Isiraeli achita manyazi,
Ngati mmene wakuba amachitira akagwidwa,
Iwowo, mafumu awo ndi akalonga awo,
Ansembe awo ndiponso aneneri awo.+
27 Iwo amauza mtengo kuti, ‘Ndinu bambo anga,’+
Ndipo mwala amauuza kuti, ‘Ndinu amene munandibereka.’
Koma ine andifulatira ndipo sanandisonyeze nkhope yawo.+
Koma tsoka likadzawagwera adzanena kuti,
‘Bwerani mudzatipulumutse!’+
28 Kodi milungu yako imene unapanga ija ili kuti?+
Imeneyo ibwere kwa iwe ngati ingathe kukupulumutsa pa nthawi ya tsoka,
Chifukwa iwe Yuda, milungu yako yachuluka mofanana ndi mizinda yako.+
29 ‘Kodi nʼchifukwa chiyani mukupitiriza kundiimba mlandu?
Nʼchifukwa chiyani nonsenu mwandipandukira?’+ akutero Yehova.
30 Ndalanga ana anu aamuna koma sizinathandize.+
31 Inu anthu anga, ganizirani mawu a Yehova.
“Kodi ine ndakhala ngati chipululu kwa Isiraeli
Kapena ngati dziko lamdima wandiweyani?
Nʼchifukwa chiyani anthu angawa anena kuti, ‘Tikungoyendayenda mmene tikufunira.
Sitibweranso kwa inuʼ?+
32 Kodi namwali angaiwale zinthu zake zodzikongoletsera?
Kodi mkwatibwi angaiwale lamba wake wapachifuwa?*
Komatu anthu anga andiiwala kwa masiku osawerengeka.+
33 Mkazi iwe wachita zinthu mwaluso pofunafuna amuna oti akukonde.
Wadziphunzitsa kuchita zinthu zoipa.+
34 Ngakhale zovala zako zathimbirira ndi magazi a anthu osauka omwe ndi osalakwa,+
Ngakhale kuti anthuwo sindinawapeze akuthyola nyumba kuti abe,
Ndaona kuti magazi awo ali pazovala zako zonse.+
35 Koma iwe ukunena kuti, ‘Ine ndilibe mlandu uliwonse.
Ndithudi mkwiyo wake wandichokera.’
Tsopano ndikukupatsa chiweruzo
Chifukwa ukunena kuti, ‘Sindinachimwe.’
36 Nʼchifukwa chiyani ukuona mopepuka kusakhulupirika kwako?
37 Pa chifukwa chimenechi, udzayenda manja ako ali kumutu,+
Chifukwa Yehova wakana amene umawadalira
Ndipo iwo sadzakuthandiza kuti zinthu zikuyendere bwino.”
3 Anthu amafunsa kuti: “Ngati mwamuna wathetsa ukwati ndi mkazi wake, ndipo mkaziyo akachokadi nʼkukakwatiwa ndi mwamuna wina, kodi mwamunayo angabwererenso kwa mkaziyo?”
Kodi dzikoli silaipitsidwa kale kwambiri?+
Yehova wanena kuti: “Iwe wachita uhule ndi amuna ambirimbiri.+
Ndiye kodi pano ukufuna ubwererenso kwa ine?
2 Yangʼana pamwamba pa mapiri ndipo uone.
Kodi ndi pamalo ati pamene amuna sanakugonerepo?
Unkakhala mʼmbali mwa njira nʼkumawadikirira
Ngati munthu wongoyendayenda* mʼchipululu.
Ukupitiriza kuipitsa dzikoli
Ndi uhule wako komanso kuipa kwako.+
3 Choncho mvula yamvumbi yaletsedwa kuti isagwe,+
Ndipo mvula yomalizira siinagwe.
Ukuchita zinthu mopanda manyazi ngati mkazi amene akuchita uhule.
Palibe chimene chikukuchititsa manyazi.+
4 Koma tsopano ukundiitana kuti:
‘Bambo anga, inu ndinu mnzanga wapamtima kuyambira pa unyamata wanga.+
5 Kodi mukhala wokwiya mpaka kalekale,
Kapena kusunga chakukhosi nthawi zonse?’
Izi ndi zimene mwanena,
Koma mukupitiriza kuchita zoipa zilizonse mmene mungathere.”+
6 Mʼmasiku a Mfumu Yosiya,+ Yehova anandiuza kuti: “‘Kodi waona zimene Isiraeli wosakhulupirikayu akuchita? Akupita kuphiri lililonse lalitali ndi pansi pa mtengo uliwonse waukulu wa masamba ambiri obiriwira kuti akachite uhule kumeneko.+ 7 Ngakhale kuti anachita zonsezi, ine ndinamupempha mobwerezabwereza kuti abwerere kwa ine,+ koma iye sanabwerere. Ndipo Yuda ankangoyangʼana zimene mchemwali wake wachinyengoyo ankachita.+ 8 Nditaona zimenezo, ndinathamangitsa Isiraeli wosakhulupirikayo ndipo ndinamupatsa kalata yotsimikizira kuti ukwati watha+ chifukwa anachita chigololo.+ Koma Yuda mchemwali wake, amene ndi wachinyengo, sanachite mantha. Nayenso anayamba kuchita uhule.+ 9 Iye ankaona kuti kuchita uhulewo si vuto moti anapitiriza kuipitsa dzikolo ndipo ankachita chigololo ndi miyala komanso mitengo.+ 10 Ngakhale kuti anachita zonsezi, mchemwali wake Yuda amene ndi wachinyengo sanabwerere kwa ine ndi mtima wake wonse, koma anangobwerera mwachiphamaso,’ akutero Yehova.”
11 Kenako Yehova anandiuza kuti: “Isiraeli amene ndi wosakhulupirika wasonyeza kuti ndi wolungama kwambiri kuposa Yuda amene ndi wachinyengo.+ 12 Pita, ndipo ukalengeze mawu awa kumpoto:+
‘Yehova wanena kuti:+ “Bwerera Isiraeli wopanduka iwe. Sindidzakuyangʼana mokwiya+ chifukwa ndine wokhulupirika,” akutero Yehova. “Sindidzakhala wokwiya mpaka kalekale. 13 Koma vomerezani kuti ndinu olakwa chifukwa mwapandukira Yehova Mulungu wanu. Munapitiriza kuchita chiwerewere ndi anthu achilendo* pansi pa mtengo uliwonse waukulu wa masamba ambiri obiriwira. Koma simunamvere mawu anga,” akutero Yehova.’”
14 “Bwererani inu ana opanduka,” akutero Yehova. “Ine ndakhala mbuye wanu* weniweni. Ine ndidzakutengani, mmodzi kuchokera mumzinda uliwonse, awiri kuchokera mʼbanja lililonse ndipo ndidzakupititsani ku Ziyoni.+ 15 Ndidzakupatsani abusa amene amachita zinthu zogwirizana ndi zofuna zanga+ ndipo adzakuthandizani kuti mudziwe zinthu zambiri ndiponso kuti mukhale omvetsa zinthu. 16 Masiku amenewo Mudzaberekana ndipo mudzakhala ambiri mʼdzikoli,” akutero Yehova.+ “Iwo sadzanenanso kuti, ‘Likasa la pangano la Yehova!’ Sadzaliganiziranso mʼmitima yawo, kulikumbukira kapena kulilakalaka ndipo sadzapanganso likasa lina. 17 Pa nthawi imeneyo mzinda wa Yerusalemu adzautchula kuti mpando wachifumu wa Yehova.+ Ndipo mitundu yonse adzaisonkhanitsa pamodzi ku Yerusalemu kuti ikatamande dzina la Yehova+ kumeneko. Iwo sadzaumitsanso khosi nʼkumatsatira mitima yawo yoipayo.
18 Mʼmasiku amenewo nyumba ya Yuda idzayenda pamodzi ndi nyumba ya Isiraeli.+ Onse pamodzi adzabwera kuchokera mʼdziko lakumpoto nʼkulowa mʼdziko limene ndinapereka kwa makolo anu kuti likhale cholowa chawo.+ 19 Ine ndinkaganiza kuti, ‘Mosangalala ndinakuika pakati pa ana aamuna nʼkukupatsa dziko labwino kwambiri, cholowa chokongola kwambiri pakati pa mitundu ya anthu!’*+ Ndinkaganizanso kuti uzindiitana kuti, ‘Bambo anga!’ ndiponso kuti sudzasiya kunditsatira. 20 ‘Ndithudi, mofanana ndi mkazi amene amasiya mwamuna wake mwachinyengo, inunso a mʼnyumba ya Isiraeli mwandichitira zachinyengo,’+ akutero Yehova.”
21 Pamwamba pa mapiri pamveka phokoso,
La kulira ndi kuchonderera kwa Aisiraeli,
Chifukwa akhotetsa njira zawo
Ndipo aiwala Yehova Mulungu wawo.+
22 “Bwererani, inu ana opanduka.
Ndidzachiritsa mtima wanu wopandukawo.”+
“Ife tabwerera! Tabwera kwa inu,
Chifukwa inu Yehova ndinu Mulungu wathu.+
23 Ndithudi, tinkangodzinamiza tokha pochitira milungu ina zikondwerero zaphokoso mʼzitunda ndi mʼmapiri.+
Kunena zoona chipulumutso cha Isiraeli chimachokera kwa Yehova Mulungu wathu.+
24 Koma chinthu chochititsa manyazi chadya* zinthu zonse zimene makolo athu anazipeza movutikira kuyambira tili anyamata.+
Chadya nkhosa zawo ndi ngʼombe zawo,
Ana awo aamuna ndi ana awo aakazi.
25 Tiyeni tigone pansi mwamanyazi,
Ndipo manyazi athuwo atiphimbe,
Chifukwa tachimwira Yehova Mulungu wathu,+
Ifeyo pamodzi ndi makolo athu kuyambira tili achinyamata mpaka pano,+
Ndipo sitinamvere mawu a Yehova Mulungu wathu.”
4 Yehova wanena kuti: “Ngati ungabwerere, iwe Isiraeli,
Ngati ungabwerere kwa ine
Ndipo ngati ungachotse mafano ako onyansa pamaso panga,
Sudzakhalanso moyo wothawathawa.+
2 Ndipo ngati ungalumbire,
Mʼchoonadi komanso mwachilungamo kuti, ‘Pali Yehova Mulungu wamoyo,’
Ndiye kuti mitundu ya anthu idzapeza madalitso kudzera mwa iye
Ndipo idzauza ena za iye monyadira.”+
3 Zimene Yehova wanena kwa anthu a ku Yuda ndi ku Yerusalemu ndi izi:
“Limani minda panthaka yabwino,
Ndipo musapitirize kudzala mbewu pakati pa minga.+
4 Chitani mdulidwe pamaso pa Yehova,
Chitani mdulidwe wa mitima yanu,+
Inu anthu a ku Yuda komanso anthu amene mukukhala mu Yerusalemu,
Kuti mkwiyo wanga usayake ngati moto,
Usayake popanda aliyense wowuzimitsa,
Chifukwa cha zochita zanu zoipa.”+
5 Nenani zimenezi mu Yuda ndipo zilengezeni mu Yerusalemu.
Fuulani ndi kuliza lipenga la nyanga ya nkhosa mʼdziko lonse.+
Fuulani ndipo nenani kuti: “Sonkhanani pamodzi,
Tiyeni tithawire mʼmizinda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri.+
6 Kwezani chizindikiro choloza njira ya ku Ziyoni.
Thawirani kumalo otetezeka, musangoima,”
Chifukwa ndikubweretsa tsoka kuchokera kumpoto,+ tsoka lalikulu kwambiri.
7 Mofanana ndi mkango umene ukutuluka paziyangoyango pamene umakhala,+
Amene akuwononga mitundu ya anthu wanyamuka.+
Wachoka mʼmalo ake kuti adzasandutse dziko lanu chinthu chochititsa mantha.
Mizinda yanu idzakhala mabwinja ndipo palibe munthu aliyense amene adzakhalemo.+
8 Choncho valani ziguduli,+
Dzigugudeni pachifuwa ndi kulira mofuula,
Chifukwa mkwiyo woyaka moto wa Yehova sunatichokere.
9 Yehova wanena kuti: “Pa tsiku limenelo mfumu sidzalimba mtima,+
Chimodzimodzinso akalonga ake.
Ansembe adzagwidwa ndi mantha ndipo aneneri adzadabwa.”+
10 Kenako ndinanena kuti: “Mayo ine Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa! Kunena zoona, mwapusitsa kwambiri anthu awa+ ndiponso Yerusalemu ponena kuti, ‘Mudzakhala pa mtendere,’+ pamene lupanga lili pakhosi pathu.”*
11 Pa nthawi imeneyo anthu awa komanso Yerusalemu adzauzidwa kuti:
“Mphepo yotentha imene ikuchokera mʼmapiri opanda kanthu amʼchipululu,
Idzaomba pamwana wamkazi wa anthu anga.
Mphepo imeneyi sikubwera kuti idzauluze mankhusu* kapena kudzayeretsa tirigu.
12 Mphepo yamphamvu ikubwera kuchokera mʼmalo amenewa chifukwa choti ine ndalamula.
Tsopano ndipereka ziweruzo kwa anthu anga.
13 Taonani! Mdani adzabwera ngati mitambo yamvula,
Ndipo magaleta ake ali ngati mphepo yamkuntho.+
Mahatchi ake ndi aliwiro kuposa ziwombankhanga.+
Tsoka latigwera chifukwa tawonongedwa.
14 Tsuka mtima wako nʼkuchotsa zoipa zonse, iwe Yerusalemu, kuti upulumuke.+
Kodi udzakhala ndi maganizo oipa mpaka liti?
15 Chifukwa mawu olengeza uthenga akumveka kuchokera ku Dani,+
Ndipo akulengeza za tsoka kuchokera kumapiri a ku Efuraimu.
16 Nenani zimenezi kwa anthu a mitundu ina.
Lengezani kuti zimenezi zidzachitikira Yerusalemu.”
“Akazitape* akubwera kuchokera kudziko lakutali
Ndipo adzalengeza mofuula zimene zidzachitikire mizinda ya Yuda.
17 Iwo aukira Yerusalemu kuchokera mbali zonse ngati alonda a kunja kwa mzinda,+
Chifukwa iye wandipandukira,”+ akutero Yehova.
18 “Udzalipira chifukwa cha khalidwe lako ndi zochita zako.+
Chilango chimenechi chidzakhala chowawa,
Chifukwa zochita zako zakhazikika mumtima mwako.”
19 Mayo ine,* mayo ine!
Ndikumva kupweteka kwambiri mumtima mwanga.
Mtima wanga ukugunda kwambiri.
Sindingathe kukhala chete,
Chifukwa ndamva kulira kwa lipenga la nyanga ya nkhosa,
20 Ndikumva uthenga wa masoka otsatizanatsatizana,
Chifukwa dziko lonse lawonongedwa.
Mwadzidzidzi matenti anga awonongedwa
Mʼkanthawi kochepa nsalu za matenti anga zawonongedwa.+
21 Kodi ndipitiriza kuona chizindikirocho,
Ndi kumva kulira kwa lipenga la nyanga ya nkhosako mpaka liti?+
22 “Anthu anga ndi opusa.+
Iwo saganizira za ine.
Ndi ana opusa ndipo samvetsa zinthu.
Amaoneka ochenjera* akamachita zoipa,
Koma sadziwa kuchita zabwino.”
23 Ndinaliona dzikolo ndipo linali lopanda kanthu komanso linangosiyidwa.+
Ndinayangʼana kumwamba ndipo sikunkawala.+
24 Ndinaona mapiri ndipo ankagwedezeka,
Ndipo zitunda zinkanjenjemera.+
25 Ndinayangʼana koma panalibe munthu aliyense,
Ndipo mbalame zonse zinali zitathawa.+
26 Ndinayangʼana ndipo ndinaona kuti munda wa zipatso unali utasanduka thengo,
Komanso mizinda yake yonse inali itagwetsedwa.+
Zimenezi zinachitika chifukwa cha Yehova,
Chifukwa cha mkwiyo wake woyaka moto.
27 Yehova wanena kuti: “Dziko lonseli lidzakhala bwinja,+
Koma sindidzaliwonongeratu.
Izi zili choncho chifukwa ndanena, ndasankha kuchita zimenezi,
Ndipo sindidzasintha maganizo anga* kapena kulephera kuchita zimenezi.+
29 Chifukwa cha phokoso la asilikali okwera pamahatchi ndiponso oponya mivi ndi uta,
Mzinda wonse wathawa.+
Alowa paziyangoyango,
Ndipo akwera mʼmatanthwe.+
Mumzinda uliwonse anthu athawamo
Ndipo palibe munthu amene akukhalamo.”
30 Popeza tsopano wawonongedwa, ndiye utani?
Unkakonda kuvala zovala zamtengo wapatali,*
Kudzikongoletsa ndi zokongoletsera zagolide
Ndiponso kukongoletsa mʼmaso mwako ndi penti wakuda.
Koma unkangotaya nthawi yako pachabe podzikongoletsa.+
Amene ankakufuna akukana
Ndipo tsopano akufuna kukupha.+
31 Ine ndamva mawu angati a mkazi amene akumva ululu,
Ndamva ngati kubuula kwa mkazi amene akubereka mwana wake woyamba,
Koma ndi mawu a mwana wamkazi wa Ziyoni* amene akupuma movutikira.
Iye akutambasula manja ake nʼkunena kuti:+
“Mayo ine, ndatopa ndi anthu amene akufuna kundipha!”
5 Yendayendani mʼmisewu ya mu Yerusalemu.
Yangʼanani mosamala kwambiri.
Fufuzani mʼmabwalo ake kuti muone
Ngati mungapeze munthu amene amachita zachilungamo,+
Amene amayesetsa kukhala wokhulupirika,
Ngati mungamupeze munthu woteroyo, ndidzaukhululukira mzinda umenewu.
2 Ngakhale atalumbira kuti: “Pali Yehova Mulungu wamoyo!”
Adzakhalabe akulumbira mwachinyengo.+
3 Inu Yehova, kodi si paja maso anu amayangʼana anthu amene ndi okhulupirika?+
Mwawalanga koma sanamve kupweteka.*
Ngakhale kuti munatsala pangʼono kuwawononga onse, iwo sanaphunzirepo kanthu.+
4 Koma ndinati: “Ndithudi, amenewa ndi anthu onyozeka.
Akuchita zinthu mopusa, chifukwa sakudziwa njira ya Yehova,
Zimene Mulungu wawo amafuna.
5 Ndidzapita kwa anthu olemekezeka nʼkulankhula nawo,
Chifukwa mosakayikira akuyenera kudziwa njira ya Yehova,
Zimene Mulungu wawo amafuna.+
Koma onsewo athyola goli la Mulungu
Ndipo adula zingwe za Mulungu.”
6 Nʼchifukwa chake mkango wa mʼnkhalango umawaukira,
Mmbulu wamʼchipululu ukupitirizabe kuwawononga,
Ndipo kambuku amakhala tcheru pamizinda yawo.
Aliyense wotuluka mʼmizindayo amakhadzulidwakhadzulidwa.
Chifukwa zolakwa zawo ndi zochuluka.
Ndipo nthawi zambiri amachita zosakhulupirika.+
7 Kodi ndingakukhululukire bwanji zinthu zimenezi?
Ana ako aamuna andisiya,
Ndipo amalumbira pa zinthu zimene si Mulungu.+
Ndinkawapatsa zimene ankafunikira,
Koma anapitiriza kuchita chigololo,
Ndipo ankapita kunyumba ya hule mʼchigulu.
8 Iwo ali ngati mahatchi amphongo achilakolako champhamvu chofuna kukwera,
9 “Kodi sindikuyenera kuwalanga chifukwa cha zinthu zimenezi?” akutero Yehova.
“Kodi sindikuyenera kubwezera mtundu wa anthu oterewa?”+
10 “Bwerani mudzaukire minda yake ya mpesa nʼkuiwononga,
Koma musaiwonongeretu.+
Dulani nthambi zake zingʼonozingʼono,
Chifukwa si za Yehova.
11 Chifukwa a mʼnyumba ya Isiraeli ndi a mʼnyumba ya Yuda
Andichitira zachinyengo kwambiri,” akutero Yehova.+
Palibe tsoka limene lidzatigwere.
Sitidzaona nkhondo kapena njala.’+
13 Aneneri akulankhula zopanda pake,
Ndipo mwa iwo mulibe mawu a Mulungu.
Nawonso adzakhala opanda pake ngati mawu awo omwewo.”
14 Choncho izi nʼzimene Yehova, Mulungu wa magulu ankhondo akumwamba akunena:
“Chifukwa anthu awa akunena zimenezi,
Ndichititsa kuti mawu anga akhale ngati moto mʼkamwa mwako,+
Koma anthu awa akhala ngati nkhuni
Ndipo motowo udzawawotcha.”+
15 “Ndikukubweretserani mtundu wa anthu kuchokera kutali, inu a mʼnyumba ya Isiraeli,”+ akutero Yehova.
“Umenewu ndi mtundu umene wakhalapo kwa nthawi yaitali,
Ndi mtundu wakale kwambiri,
Mtundu umene chilankhulo chake simukuchidziwa,
Ndipo simungamve zimene amalankhula.+
16 Kachikwama kawo koikamo mivi kali ngati manda otseguka.
Onse ndi asilikali.
17 Iwo adzadya zokolola zanu ndi zakudya zanu.+
Adzadya ana anu aamuna ndi ana anu aakazi.
Adzadya nkhosa zanu ndi ngʼombe zanu.
Adzadya mitengo yanu ya mpesa ndi mitengo yanu ya mkuyu.
Iwo adzawononga ndi lupanga mizinda yanu imene mumaidalira, yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri.”
18 Yehova wanena kuti: “Ngakhale masiku amenewo, sindidzakuwonongani nonse.+ 19 Ndiye akadzafunsa kuti, ‘Nʼchifukwa chiyani Yehova Mulungu wathu watichitira zinthu zonsezi?’ udzawayankhe kuti, ‘Mofanana ndi mmene munandisiyira nʼkukatumikira mulungu wachilendo mʼdziko lanu, mudzatumikiranso alendo mʼdziko limene si lanu.’”+
20 Ukanene izi mʼnyumba ya Yakobo,
Ndipo ukazilengeze mu Yuda kuti:
21 “Tamverani izi anthu opusa komanso opanda nzeru inu:*+
22 ‘Kodi simukuchita nane mantha?’ akutero Yehova.
‘Kodi simukunjenjemera pamaso panga?
Ine ndi amene ndinaika mchenga kuti ukhale malire a nyanja,
Malire amene adzakhalepo mpaka kalekale.
Ngakhale kuti mafunde ake amawinduka, sangadutse malirewo.
Ndipo ngakhale amachita phokoso, sangapitirire malirewo.+
23 Koma anthu awa ali ndi mtima wosamvera komanso wopanduka.
Achoka panjira yanga ndipo akuyenda mʼnjira yawo.+
24 Mumtima mwawo sanena kuti:
“Tiyeni tsopano tiope Yehova Mulungu wathu,
Amene amatigwetsera mvula mʼnyengo yake,
Amatigwetsera mvula yoyamba ndi yomalizira,
25 Zolakwa zanu ndi zimene zachititsa kuti zinthu zimenezi zisabwere,
Ndipo machimo anu akumanitsani zinthu zabwino.+
26 Chifukwa pakati pa anthu anga pali anthu oipa.
Iwo amabisala nʼkumayangʼanitsitsa ngati mmene amachitira wosaka mbalame.
Amatchera msampha wakupha
Ndipo amagwira anthu.
27 Mofanana ndi chikwere chimene chadzaza mbalame,
Nyumba zawo zadzaza chinyengo.+
Nʼchifukwa chake iwo ali amphamvu komanso alemera kwambiri.
28 Iwo anenepa ndipo asalala.
Akuchita zinthu zoipa zambiri.
Iwo saweruza mlandu wa ana amasiye mwachilungamo,+
Pofuna kupeza phindu.
Ndipo sachitira chilungamo anthu osauka.’”+
29 “Kodi sindikuyenera kuwalanga chifukwa cha zinthu zimenezi?” akutero Yehova.
“Kodi sindikuyenera kubwezera mtundu wa anthu oterewa?
30 Chinthu chodabwitsa komanso chochititsa mantha chachitika mʼdziko:
31 Aneneri akulosera zabodza,+
Ndipo ansembe akugwiritsa ntchito mphamvu zawo kuti azilamulira ena.
Anthu anga nawonso akukonda zimenezi.+
Koma kodi mudzachita chiyani mapeto akadzafika?”
6 Bisalani inu ana a Benjamini, thawani mu Yerusalemu.
Chifukwa tsoka likubwera kuchokera kumpoto ndipo ndi lalikulu kwambiri.+
2 Mwana wamkazi wa Ziyoni* akufanana ndi mkazi wokongola komanso wosasatitsidwa.+
3 Abusa ndi magulu awo a ziweto adzabwera.
4 “Konzekerani* kukachita nkhondo ndi Yerusalemu
Nyamukani, tiyeni tikamuukire dzuwa lili paliwombo!”
“Koma tachita tsoka chifukwa nthawi yatithera,
Ndipo kunja kwayamba kuda!”
5 “Nyamukani, tiyeni tikamuukire usiku
Ndipo tikawononge nsanja zake zokhala ndi mipanda yolimba.”+
6 Chifukwa Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti:
“Dulani mitengo kuti timange malo okwera oti timenyerepo nkhondo* ndi Yerusalemu.+
Yerusalemu ndi mzinda umene ukuyenera kuimbidwa mlandu.
Mkati mwake muli kuponderezana kokhakokha.+
7 Mofanana ndi chitsime chimene chimatulutsa madzi ozizira,
Yerusalemu amatulutsanso zinthu zoipa.
Mkati mwake mukumveka phokoso la chiwawa komanso kuponderezana.+
Nthawi zonse ndimaona matenda ndi miliri mumzindawo.
8 Iwe Yerusalemu, mvera chenjezo langa, ukapanda kumvera, ndikusiya chifukwa chonyansidwa nawe.+
Ndidzakusandutsa bwinja, dziko lopanda munthu aliyense wokhalamo.”+
9 Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti:
“Adani adzakunkha otsalira onse a Isiraeli ngati mmene amakunkhira mphesa zomaliza pa mtengo wa mpesa.
Kwezanso dzanja lako ngati munthu amene akuthyola mphesa panthambi za mtengo wa mpesa.”
10 “Kodi ndilankhule ndi ndani nʼkumuchenjeza?
Ndi ndani adzamvetsere?
Taonani! Makutu awo ndi otseka,* choncho sangathe kumva.+
Taonani! Mawu a Yehova akhala chinthu chimene akunyansidwa nacho+
Ndipo sakusangalala nawo.
11 Ndadzazidwa ndi mkwiyo wa Yehova,
Ndipo ndatopa ndi kuusunga.”+
“Tsanulirani mkwiyowo pa mwana amene ali mumsewu,+
Pa gulu la anyamata amene asonkhana pamodzi.
Onse adzagwidwa, mwamuna limodzi ndi mkazi wake,
Anthu achikulire limodzi ndi anthu okalamba.+
12 Nyumba zawo limodzi ndi minda yawo komanso akazi awo,
Zidzaperekedwa kwa anthu ena.+
Chifukwa ndidzatambasula dzanja langa nʼkuwononga anthu okhala mʼdzikolo,” akutero Yehova.
13 “Chifukwa aliyense kuyambira wamngʼono mpaka wamkulu, akupeza phindu mwachinyengo.+
Kuyambira mneneri mpaka wansembe, aliyense akuchita zachinyengo.+
14 Iwo akuyesa kuchiritsa mwachinyengo kuwonongeka kwa anthu anga* ponena kuti,
‘Kuli mtendere! Kuli mtendere!’
Pamene kulibe mtendere.+
15 Kodi iwo amachita manyazi ndi zinthu zonyansa zimene achita?
Iwo sachita manyazi ngakhale pangʼono,
Ndipo sadziwa nʼkomwe kuchita manyazi.+
Choncho iwo adzagwa pamodzi ndi anthu amene akugwa.
Ndikamadzawapatsa chilango, iwo adzapunthwa,” akutero Yehova.
16 Yehova wanena kuti:
“Imani pamphambano kuti muone.
Funsani zokhudza njira zakale,
Funsani kuti mudziwe kumene kuli njira yabwino nʼkuyenda mmenemo,+
Kuti mupeze mpumulo.”
Koma iwo akunena kuti: “Ife sitiyenda mʼnjira imeneyo.”+
Koma iwo ananena kuti: “Ife sitidzamvera.”+
18 “Choncho tamverani, inu mitundu ya anthu,
Kuti mudziwe anthu inu,
Zimene zidzachitikire anthu a ku Yerusalemu.
19 Tamverani, inu anthu okhala padziko lapansi!
Ine ndikubweretsa tsoka pa anthu awa+
Chifukwa cha maganizo awo oipa.
Iwo sanamvere mawu anga
Ndipo anakana chilamulo changa.”*
20 “Kodi lubani* wochokera ku Sheba
Komanso bango lonunkhira lochokera kudziko lakutali zimene mukundibweretsera, zili ndi phindu lanji kwa ine?
Nsembe zanu zopsereza zathunthu nʼzosavomerezeka,
Ndipo nsembe zanu zina zonse zimene mukupereka sizikundisangalatsa.”+
21 Choncho Yehova wanena kuti:
“Tsopano ndikuikira anthu awa zinthu zopunthwitsa,
Ndipo iwo adzapunthwa ndi zinthu zimenezi,
Abambo limodzi ndi ana,
Munthu ndi mnzake woyandikana naye,
Onse adzawonongedwa.”+
22 Yehova wanena kuti:
“Taonani! Anthu akubwera kuchokera kudziko lakumpoto.
Ndipo mtundu wamphamvu udzadzutsidwa kuchokera kumadera akutali kwambiri a dziko lapansi.+
23 Iwo adzagwira uta ndi nthungo.
Amenewa ndi anthu ankhanza ndipo sadzasonyeza chifundo.
Mawu awo adzamveka ngati mkokomo wa nyanja
Ndipo adzabwera pamahatchi.+
Iwo afola mwa dongosolo lomenyera nkhondo ngati mwamuna wankhondo kuti amenyane nawe, iwe mwana wamkazi wa Ziyoni.”
24 Ife tamva uthenga wokhudza zimenezi.
25 Musatuluke kupita kunja,
Ndipo musayende mumsewu,
Chifukwa mdani ali ndi lupanga.
Zochititsa mantha zili paliponse.
26 Iwe mwana wamkazi wa anthu anga,
Vala chiguduli+ ndipo ugubuduke mʼphulusa.
Lira ngati kuti ukulira maliro a mwana wamwamuna mmodzi yekhayo, ulire mowawidwa mtima,+
Chifukwa wowononga adzatiukira modzidzimutsa.+
27 “Ndakusandutsa* woyenga zitsulo pakati pa anthu anga,
Ndakusandutsa wofufuza mosamala.
Choncho uzionetsetsa ndiponso kufufuza njira zawo.
Iwo ali ngati kopa* ndi chitsulo,
Onsewo ndi anthu achinyengo.
29 Zipangizo zopemerera moto zapsa ndi moto.
Ndipo pamotopo patuluka mtovu.
Munthu wakhala akuyenga chitsulo mobwerezabwereza koma osaphula kanthu,+
Ndipo zoipa sizinachotsedwemo.+
30 Ndithu, anthu adzawatchula kuti siliva wokanidwa,
Chifukwa Yehova wawakana.”+
7 Awa ndi mawu amene Yehova anauza Yeremiya. Iye anamuuza kuti: 2 “Ukaime pageti la nyumba ya Yehova ndipo ukalengeze uthenga uwu, ‘Tamverani mawu a Yehova inu anthu nonse a mu Yuda, amene mumalowa pamageti awa kuti mukalambire Yehova. 3 Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Mulungu wa Isiraeli wanena kuti: “Sinthani njira zanu komanso zochita zanu ndipo muzichita zabwino. Mukatero ine ndidzakulolani kuti mupitirize kukhala mʼdziko lino.+ 4 Musamakhulupirire mawu achinyengo nʼkumanena kuti, ‘Uyu* ndi kachisi wa Yehova, inde ndi kachisi wa Yehova, ndithudi ndi kachisi wa Yehova!’+ 5 Ngati mutasinthadi njira zanu ndi zochita zanu kuti zikhale zabwino, ngati mutamaweruza mwachilungamo pakati pa munthu ndi mnzake,+ 6 ngati simudzapondereza alendo okhala pakati panu, ana amasiye ndi akazi amasiye,+ komanso ngati simudzakhetsa magazi a munthu wosalakwa mʼdziko lino ndiponso ngati simudzatsatira milungu ina, zimene zingakubweretsereni mavuto,+ 7 inenso ndidzakulolani kuti mupitirize kukhala mʼdziko lino, dziko limene ndinapatsa makolo anu, kuti azikhalamo mpaka kalekale.”’”
8 “Koma inu mukukhulupirira mawu achinyengo+ ndipo sakuthandizani ngakhale pangʼono. 9 Kodi mungamabe,+ kupha, kuchita chigololo, kulumbira monama,+ kupereka nsembe* kwa Baala+ ndiponso kutsatira milungu ina imene simunkaidziwa, 10 kenako nʼkubwera kudzaima pamaso panga mʼnyumba iyi, imene imatchedwa ndi dzina langa nʼkumanena kuti, ‘Tidzapulumutsidwa,’ ngakhale kuti mukuchita zinthu zonyansa zonsezi? 11 Kodi nyumba iyi, imene imatchedwa ndi dzina langa, mwayamba kuiona ngati phanga la achifwamba?+ Inetu ndaona zimene mukuchita,” akutero Yehova.
12 “‘Pitani kumalo anga ku Silo,+ kumene poyamba kunali dzina langa,+ ndipo mukaone zimene ndinachitira malowo chifukwa cha kuipa kwa anthu anga Aisiraeli.+ 13 Koma inu munapitiriza kuchita zinthu zonsezi,’ akutero Yehova, ‘ndipo ngakhale kuti ndinkalankhula nanu mobwerezabwereza,* inu simunamvere.+ Ndinapitiriza kukuitanani koma inu simunayankhe.+ 14 Choncho nyumba imene ikudziwika ndi dzina langa,+ imene mukuidalira+ ndiponso pamalo awa amene ndinawapereka kwa inu ndi makolo anu, ndidzachita zofanana ndi zimene ndinachita ku Silo.+ 15 Ine ndidzakuchotsani pamaso panga ngati mmene ndinachotsera abale anu onse, mbadwa zonse za Efuraimu.’+
16 Koma iwe usawapempherere anthu awa. Usafuule kwa ine, kuwapempherera kapena kundichonderera kuti ndiwathandize,+ chifukwa ine sindidzakumvetsera.+ 17 Kodi sukuona zimene akuchita mʼmizinda ya Yuda ndi mʼmisewu ya mu Yerusalemu? 18 Ana aamuna akutola nkhuni, abambo akuyatsa moto ndipo akazi awo akukanda ufa kuti apange makeke okapereka nsembe kwa ‘Mfumukazi Yakumwamba.’*+ Ndipo akuthira pansi nsembe zachakumwa kwa milungu ina kuti andikhumudwitse.+ 19 ‘Koma kodi iwo akukhumudwitsa ine?’ akutero Yehova. ‘Kodi iwo sakudzikhumudwitsa okha nʼkudzichititsa manyazi?’+ 20 Choncho Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Taonani! Mkwiyo wanga ndi ukali wanga zidzatsanulidwa pamalo awa,+ pamunthu, pachiweto, pamitengo yakuthengo ndi pachipatso chilichonse chochokera mʼnthaka. Mkwiyowo udzayaka ndipo sudzazimitsidwa.’+
21 Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti, ‘Wonjezerani nsembe zanu zopsereza zathunthu pansembe zanu zinazo ndipo muzidye nokha.+ 22 Chifukwatu pa tsiku limene ndinatulutsa makolo anu mʼdziko la Iguputo, sindinalankhule nawo chilichonse kapena kuwalamula zokhudza kupereka nsembe zopsereza zathunthu ndi nsembe zina.+ 23 Koma ndinawalamula kuti: “Muzimvera mawu anga, ndipo ndidzakhala Mulungu wanu, inuyo mudzakhala anthu anga.+ Muziyenda mʼnjira imene ndakulamulani, kuti zinthu zikuyendereni bwino.”’+ 24 Koma iwo sanamvere kapena kutchera khutu.+ Mʼmalomwake, anayenda motsatira zofuna zawo. Mouma khosi anatsatira zofuna za mtima wawo woipawo,+ moti anabwerera mʼmbuyo mʼmalo mopita patsogolo, 25 kuchokera tsiku limene makolo anu anatuluka mʼdziko la Iguputo mpaka pano.+ Choncho ndinapitiriza kukutumizirani atumiki anga onse omwe ndi aneneri, ndinkawatumiza tsiku lililonse, mobwerezabwereza.*+ 26 Koma iwo anakana kundimvera ndipo sanatchere khutu lawo.+ Mʼmalomwake anaumitsa khosi lawo ndipo ankachita zinthu zoipa kuposa makolo awo.
27 Udzawauza mawu onsewa,+ koma iwo sadzakumvera. Udzawaitana koma sadzakuyankha. 28 Ndipo udzawauze kuti, ‘Uwu ndi mtundu wa anthu umene sunamvere mawu a Yehova Mulungu wawo, ndipo anakana kulandira malangizo.* Palibe munthu wokhulupirika pakati pawo ndipo satchulanso nʼkomwe za kukhulupirika.’*+
29 Meta tsitsi lako lalitalilo* nʼkulitaya ndipo ukwere pamapiri opanda mitengo nʼkukaimba nyimbo yoimba polira, chifukwa Yehova wakana ndiponso wasiya mʼbadwo uwu umene wamukwiyitsa. 30 ‘Chifukwa mbadwa za Yuda zachita zinthu zoipa mʼmaso mwanga,’ akutero Yehova. ‘Aika mafano awo onyansa mʼnyumba imene imadziwika ndi dzina langa nʼcholinga choti aidetse.+ 31 Iwo amanga malo okwera ku Tofeti, mʼChigwa cha Mwana wa Hinomu,*+ kuti aziwotcha ana awo aamuna ndi ana awo aakazi pamoto,+ chinthu chimene sindinawalamule kuti azichita ndiponso chimene sindinachiganizirepo mumtima mwanga.’*+
32 ‘Choncho taonani! Masiku akubwera,’ akutero Yehova, ‘pamene sadzatchulanso malowo kuti Tofeti kapena kuti Chigwa cha Mwana wa Hinomu,* koma adzawatchula kuti Chigwa Chopherako Anthu. Iwo adzaika anthu mʼmanda ku Tofeti mpaka malo onse adzatha.+ 33 Mitembo ya anthu awa idzakhala chakudya cha mbalame zouluka mumlengalenga ndi cha zilombo ndipo sipadzakhala woziopseza.+ 34 Ndidzathetsa phokoso lachikondwerero, phokoso lachisangalalo, mawu a mkwati ndi mawu a mkwatibwi,+ mʼmizinda ya Yuda ndi mʼmisewu ya Yerusalemu, chifukwa dzikoli lidzawonongedwa nʼkukhala mabwinja okhaokha.’”+
8 “Pa nthawi imeneyo,” akutero Yehova, “mafupa a mafumu a Yuda, a akalonga awo, a ansembe, a aneneri ndi a anthu okhala mu Yerusalemu adzatulutsidwa mʼmanda awo. 2 Mafupawo adzamwazidwa padzuwa, pamwezi ndi panyenyezi zonse zakumwamba* zimene ankazikonda, kuzitumikira, kuzitsatira, kuzifunafuna ndi kuzigwadira.+ Anthu sadzasonkhanitsa mafupawo pamodzi nʼkuwaika mʼmanda ndipo adzakhala ngati manyowa panthaka.”+
3 “Ndipo anthu onse otsala a banja loipali amene adzapulumuke adzaona kuti ndi bwino kufa kusiyana ndi kukhala ndi moyo, malo onse amene ndidzawabalalitsire,” akutero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.
4 “Ndipo ukawauze kuti, ‘Yehova wanena kuti:
“Kodi munthu akagwa sadzukanso?
Ngati munthu mmodzi atabwerera, kodi winayo sangabwererenso?
5 Nʼchifukwa chiyani anthu awa, anthu okhala mu Yerusalemu, ali osakhulupirika ndipo akhalabe osakhulupirika kwa nthawi yaitali chonchi?
Iwo akupitiriza kuchita zachinyengo
Ndipo akukana kubwerera.+
6 Ine ndinatchera khutu ndipo ndinapitiriza kuwamvetsera. Koma zimene iwo ankanena sizinali zoona.
Panalibe munthu amene analapa zoipa zimene ankachita, kapena amene anafunsa kuti, ‘Nʼchiyani chimene ndachitachi?’+
Aliyense akungobwerera kunjira imene anthu ambiri akuitsatira, ngati hatchi imene ikuthamangira kunkhondo.
7 Ngakhale dokowe, mbalame youluka mumlengalenga, imadziwa bwino nthawi yake yoikidwiratu.
Ndipo njiwa, namzeze komanso mbalame zina, zimadziwa nthawi yobwerera kumene zachokera.*
Koma anthu anga sakudziwa chiweruzo cha Yehova.”’+
8 Kodi munganene bwanji kuti: “Ndife anzeru, ndipo tili ndi chilamulo cha Yehova”?*
Pamene zoona zake nʼzakuti zolembera zabodza+ za alembi zagwiritsidwa ntchito polemba zachinyengo.
9 Anthu anzeru achititsidwa manyazi.+
Achita mantha ndipo adzagwidwa.
Taonani! Iwo akana mawu a Yehova.
Ndipo kodi ali ndi nzeru zotani?
10 Choncho akazi awo ndidzawapereka kwa amuna ena,
Minda yawo ndidzaipereka kwa anthu ena.+
Chifukwa kuyambira wamngʼono mpaka wamkulu, aliyense akupeza phindu mwachinyengo.+
Kuyambira mneneri mpaka wansembe, aliyense akuchita zachinyengo.+
11 Iwo akuyesa kuchiritsa mwachinyengo kuwonongeka kwa mwana wamkazi* wa anthu anga ponena kuti,
‘Kuli mtendere! Kuli mtendere!’
Pamene kulibe mtendere.+
12 Kodi iwo amachita manyazi ndi zinthu zonyansa zimene achita?
Iwo sachita manyazi ngakhale pangʼono,
Ndipo sadziwa nʼkomwe kuchita manyazi.+
Choncho iwo adzagwa pamodzi ndi anthu amene akugwa.
Ndikamadzawapatsa chilango, iwo adzapunthwa,”+ akutero Yehova.
13 “‘Ndikadzawasonkhanitsa, ndidzawawononga,’ akutero Yehova.
‘Mumtengo wa mpesa simudzapezeka mphesa zotsala, mumtengo wa mkuyu simudzapezeka nkhuyu ndipo masamba adzafota.
Zinthu zimene ndinawapatsa zidzatayika.’”
14 “Nʼchifukwa chiyani tikungokhala pano?
Tiyeni tisonkhane pamodzi ndipo tilowe mʼmizinda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri+ kuti tikafere kumeneko.
Chifukwa Yehova Mulungu wathu adzatiwononga,
Ndipo amatipatsa madzi apoizoni kuti timwe,+
Chifukwa tachimwira Yehova.
15 Timayembekezera mtendere, koma palibe chabwino chilichonse chimene chachitika.
Timayembekezera kuchiritsidwa, koma tikungoona zinthu zochititsa mantha.+
16 Mahatchi ake akumveka kupuma mwawefuwefu ali ku Dani.
Dziko lonse lagwedezeka
Chifukwa cha phokoso la kumemesa* kwa mahatchi ake amphongo.
Adani akubwera kudzawononga dziko ndi chilichonse chimene chili mmenemo,
Mzinda ndi anthu okhala mmenemo.”
17 “Ine ndikutumiza njoka pakati panu,
Njoka zapoizoni zimene simungazinyengerere kuti muziseweretse,
Ndipo zidzakulumani ndithu,” akutero Yehova.
18 Chisoni changa nʼchosachiritsika.
Mtima wanga ukudwala.
19 Pakumveka mawu olirira thandizo kuchokera kudziko lakutali,
Kuchokera kwa mwana wamkazi wa anthu anga.
Iye akuti: “Kodi Yehova sali mu Ziyoni?
Kapena kodi mfumu yake mulibe mmenemo?”
“Nʼchifukwa chiyani andikhumudwitsa ndi mafano awo ogoba,
Ndiponso milungu yawo yachilendo yopanda pake?”
20 “Nthawi yokolola yadutsa ndipo nyengo yachilimwe yatha.
Koma ife sitinapulumutsidwe!”
21 Ndasweka mtima chifukwa cha kuwonongeka kwa mwana wamkazi wa anthu anga.+
Ndine wachisoni.
Ndipo ndili ndi mantha aakulu.
22 Kodi mu Giliyadi mulibe mafuta a basamu?+
Kapena kodi mulibe wochiritsa* mmenemo?+
Nʼchifukwa chiyani mwana wamkazi wa anthu anga sanachiritsidwe?+
9 Ndikanakonda mʼmutu mwanga mukanakhala madzi ambiri,
Ndiponso maso anga akanakhala kasupe wa misozi.+
Zikanatero, ndikanalira masana ndi usiku
Chifukwa cha anthu a mtundu wanga amene aphedwa.
2 Ndikanakonda ndikanakhala ndi malo ogona anthu apaulendo mʼchipululu.
Zikanatero, ndikanasiya anthu a mtundu wanga nʼkuwachokera,
Chifukwa onse ndi achigololo,+
Gulu la anthu ochita zachinyengo.
3 Iwo ndi okonzeka kunama ngati uta umene wakungidwa.
Dzikolo ladzaza ndi chinyengo ndipo palibe amene ali wokhulupirika.+
“Iwo akuchita zoipa motsatizanatsatizana,
Ndipo akundinyalanyaza,”+ akutero Yehova.
4 “Aliyense asamale ndi mnzake,
Ndipo musamakhulupirire ngakhale mʼbale wanu.
5 Aliyense amapusitsa mnzake,
Ndipo palibe amene amalankhula zoona.
Aphunzitsa lilime lawo kulankhula chinyengo.+
Iwo amadzitopetsa okha pochita zinthu zoipa.
6 Iwe ukukhala pakati pa anthu achinyengo.
Iwo anakana kundidziwa chifukwa cha chinyengo chawo,” akutero Yehova.
7 Choncho, Yehova wa magulu ankhondo akumwamba akuti:
“Ine ndidzawayenga komanso kuwayesa,+
Nanga mwana wamkazi wa anthu anga ndingamuchitirenso chiyani?
8 Lilime lawo ndi muvi wakupha umene umalankhula zachinyengo.
Munthu amalankhula mwamtendere ndi mnzake,
Koma mumtima mwake amakonza chiwembu.”
9 “Kodi sindikuyenera kuwalanga chifukwa cha zinthu zimenezi?” akutero Yehova.
“Kodi sindikuyenera kubwezera mtundu wa anthu oterewa?+
10 Ndidzalirira mapiri mokweza komanso modandaula
Ndipo ndidzaimba nyimbo yoimba polira, polirira malo odyetserako ziweto amʼchipululu,
Chifukwa awotchedwa moti palibe munthu amene angadutsemo,
Ndipo kulira kwa ziweto sikukumveka.
Mbalame zouluka mumlengalenga komanso nyama zakutchire zathawamo ndipo zachoka.+
11 Yerusalemu ndidzamusandutsa milu ya miyala+ ndiponso malo obisalamo mimbulu,+
Ndipo mizinda ya Yuda ndidzaisandutsa mabwinja, popanda wokhalamo.+
12 Kodi wanzeru ndi ndani kuti amvetse zimenezi,
Kodi Yehova walankhula ndi ndani kuti anene zimenezi?
Nʼchifukwa chiyani dzikoli lawonongedwa?
Nʼchifukwa chiyani lawotchedwa nʼkukhala ngati chipululu
Chimene palibe munthu amene akudutsamo?”
13 Yehova anayankha kuti: “Nʼchifukwa chakuti iwo asiya chilamulo changa chimene ndinawapatsa.* Komanso chifukwa chakuti sanatsatire chilamulocho ndiponso kumvera mawu anga. 14 Mʼmalo mwake, anatsatira zofuna za mitima yawo mouma khosi+ ndipo anatsatira mafano a Baala, mogwirizana ndi zimene makolo awo anawaphunzitsa.+ 15 Choncho Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti, ‘Ine ndidzadyetsa anthu amenewa chitsamba chowawa ndipo ndidzawamwetsa madzi apoizoni.+ 16 Ndidzawamwaza pakati pa mitundu ya anthu imene iwo kapena makolo awo sanaidziwe.+ Ndipo ndidzawatumizira adani awo kuti awathamangitse ndi lupanga mpaka nditawawononga onse.’+
17 Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti,
‘Chitani zinthu mozindikira.
Itanani akazi oimba nyimbo zoimba polira kuti abwere.+
Ndipo tumizani anthu kuti akaitane akazi odziwa kulira maliro,
18 Kuti abwere mofulumira nʼkudzatiimbira nyimbo zoimba polira,
Kuti maso athu atuluke misozi
Ndipo madzi atuluke mʼzikope zathu.+
19 Chifukwa ku Ziyoni kwamveka anthu akulira mofuula kuti:+
“Tawonongedwa kwambiri!
Tachita manyazi kwambiri!
Chifukwa tasiya dziko lathu ndipo atigwetsera nyumba zathu.”+
20 Akazi inu, tamverani mawu a Yehova.
Tcherani khutu kuti mumve mawu otuluka mʼkamwa mwake.
Phunzitsani ana anu aakazi kulira maliro
Ndipo aliyense aphunzitse mnzake nyimbo yoimba polirayi.+
21 Chifukwa imfa yatilowera mʼnyumba kudzera mʼmawindo.
Yalowa munsanja zathu zokhala ndi makoma olimba
Kuti mumsewu musapezeke mwana aliyense
Ndiponso kuti anyamata asapezeke mʼmabwalo a mzinda.’+
22 Unene kuti, ‘Yehova wanena kuti:
“Mitembo ya anthu idzangoti mbwee panthaka ngati manyowa.
Idzakhala ngati tirigu amene angomumweta kumene
Koma popanda munthu womusonkhanitsa pamodzi.”’”+
23 Yehova wanena kuti:
“Munthu wanzeru asadzitame chifukwa cha nzeru zake.+
Munthu wamphamvu asadzitame chifukwa cha mphamvu zake.
Ndipo munthu wachuma asadzitame chifukwa cha chuma chake.”+
24 “Koma amene akudzitama adzitame pa chifukwa chakuti:
Amamvetsa bwino njira zanga ndipo amandidziwa,+
Kuti ine ndine Yehova, amene ndimasonyeza chikondi chokhulupirika ndipo ndimachita zinthu zachilungamo komanso zolungama padziko lapansi,+
Chifukwa zinthu zimenezi zimandisangalatsa,”+ akutero Yehova.
25 Yehova wanena kuti, “Taona masiku akubwera ndipo ndidzaimba mlandu aliyense wodulidwa koma amene sanachite mdulidwe wa mtima wake.+ 26 Ndidzaimba mlandu Iguputo,+ Yuda,+ Edomu,+ Aamoni+ ndi Mowabu+ komanso onse odulira ndevu zawo zamʼmbali amene amakhala mʼchipululu.+ Chifukwa mitundu yonse ndi yosadulidwa ndipo anthu onse a mʼnyumba ya Isiraeli sanachite mdulidwe wa mitima yawo.”+
10 Inu a mʼnyumba ya Isiraeli, imvani chenjezo limene Yehova wakupatsani. 2 Yehova wanena kuti:
“Musaphunzire miyambo ya anthu a mitundu ina,+
Ndipo musachite mantha ndi zizindikiro zakumwamba,
Chifukwa anthu a mitundu ina amachita mantha ndi zizindikirozo.+
3 Miyambo ya anthu amenewa ndi yopanda pake.
4 Akatero amakongoletsa fanolo ndi siliva komanso golide.+
Kenako amatenga hamala ndi misomali nʼkulikhomerera pansi kuti lisagwe.+
5 Mafanowo ali ngati choopsezera mbalame mʼmunda wa minkhaka ndipo sangalankhule.+
Iwo amafunika kunyamulidwa chifukwa sangayende okha.+
Musamachite mantha ndi mafano chifukwa sangakuvulazeni,
Komanso sangachite chilichonse chabwino.”+
6 Palibe aliyense amene angafanane ndi inu Yehova.+
Inu ndinu wamkulu ndipo dzina lanu ndi lalikulu komanso lamphamvu.
7 Kodi ndi ndani amene sakuyenera kukuopani, inu Mfumu ya mitundu yonse?+ Inuyo ndinu woyenera kuopedwa.
Chifukwa pakati pa anzeru onse a mʼmitundu ya anthu ndiponso pakati pa maufumu awo onse,
Palibiretu aliyense wofanana ndi inu.+
8 Onse ndi opanda nzeru ndiponso opusa.+
Malangizo ochokera pamtengo amalimbikitsa anthu kuchita zachabechabe.+
9 Siliva amene anamusula kukhala mapalemapale amachokera ku Tarisi+ ndipo golide amachokera ku Ufazi.
Zonsezi zimakonzedwa mwaluso ndipo ndi ntchito ya manja a mmisiri wa zitsulo.
Amawaveka zovala zaulusi wabuluu ndi ubweya wa nkhosa wapepo.
Mafano onsewo amapangidwa ndi amisiri aluso.
10 Koma Yehova ndi Mulungu woonadi.
Iye ndi Mulungu wamoyo+ ndipo ndi Mfumu yamuyaya.+
Dziko lapansi lidzagwedezeka chifukwa cha mkwiyo wake,+
Ndipo palibe mitundu ya anthu imene idzapilire mkwiyo wake.
11* Mitunduyo ukaiuze izi:
“Milungu imene sinapange kumwamba ndi dziko lapansi
Idzawonongedwa padziko lapansi komanso pansi pa thambo.”+
12 Iye ndi Mulungu amene anapanga dziko lapansi pogwiritsa ntchito mphamvu zake,
Amene anakhazikitsa dziko lapansi pogwiritsa ntchito nzeru zake.+
Amenenso anatambasula kumwamba chifukwa cha kuzindikira kwake.+
13 Mawu ake akamveka,
Madzi akumwamba amachita mkokomo,+
Ndipo amachititsa mitambo* kukwera kuchokera kumalekezero a dziko lapansi.+
Iye amachititsa kuti kukamagwa mvula mphezi zizingʼanima,
Ndipo amatulutsa mphepo mʼnyumba zake zosungira.+
14 Munthu aliyense akuchita zinthu mopanda nzeru komanso mosazindikira.
Mmisiri wa zitsulo aliyense adzachita manyazi chifukwa cha chifaniziro chake chosula.+
Chifukwa chifaniziro chake chopangidwa ndi chitsulo chosungunula ndi mulungu wonama
15 Iwo ndi achabechabe, oyenera kunyozedwa.+
Tsiku loti aweruzidwe likadzafika adzawonongedwa.
16 Koma Mulungu, amene ndi cholowa cha Yakobo, sali ngati mafano amenewa,
Chifukwa iye ndi amene anapanga china chilichonse,
Ndipo Isiraeli ndi ndodo ya cholowa chake.+
Dzina lake ndi Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.+
17 Iwe mkazi amene wazunguliridwa ndi adani,
Sonkhanitsa katundu wako.
18 Chifukwa Yehova wanena kuti:
“Pa nthawi ino ndikuthamangitsa* anthu okhala mʼdzikoli,+
Ndipo ndidzachititsa kuti akumane ndi mavuto.”
19 Tsoka kwa ine chifukwa cha kuwonongedwa kwanga!*+
Bala langa ndi losachiritsika.
Ndinanena kuti: “Ndithudi amenewa ndi matenda anga ndipo ndikufunika kuwapirira.
20 Tenti yanga yawonongedwa ndipo zingwe zanga zonse zomangira tentiyo aziduladula.+
Ana anga aamuna andisiya ndipo kulibenso.+
Palibe aliyense amene watsala woti atambasule tenti yanga kapena kudzutsa nsalu za tentiyo.
Nʼchifukwa chake sanachite zinthu mozindikira,
Ndipo ziweto zawo zonse zabalalika.”+
22 Tamvetserani, mdani akubwera!
Kukumveka kugunda kwakukulu kuchokera kudziko lakumpoto,+
Kumene kudzasandutsa mizinda ya Yuda kukhala mabwinja, malo obisalamo mimbulu.+
23 Ine ndikudziwa bwino, inu Yehova, kuti munthu alibe ulamuliro wosankha yekha njira ya moyo wake.
Munthu amene akuyenda alibe ulamuliro wowongolera mapazi ake.+
25 Tsanulirani mkwiyo wanu pa mitundu ya anthu amene akukunyalanyazani,+
Komanso pa mafuko amene saitana pa dzina lanu.
Chifukwa iwo awononga mbadwa zonse za Yakobo,+
Amuwononga mpaka kufika potheratu,+
Ndipo dziko lake alisandutsa bwinja.+
11 Mawu amene Yehova anauza Yeremiya ndi awa: 2 “Imvani mawu a pangano langa, anthu inu!
Anthu a ku Yuda komanso okhala mu Yerusalemu ukawauze* mawu amenewa. 3 Ukawauze kuti, ‘Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti: “Munthu aliyense wosamvera mawu a mʼpangano limeneli ndi wotembereredwa.+ 4 Makolo anu ndinawalamula kuti azimvera mawu amenewa pamene ndinkawatulutsa mʼdziko la Iguputo,+ pamene ndinkawatulutsa mʼngʼanjo yosungunulira zitsulo.+ Ndinawalamula kuti, ‘Muzimvera mawu anga, ndipo muzichita zinthu zonse zimene ndakulamulani. Mukatero mudzakhala anthu anga ndipo ine ndidzakhala Mulungu wanu,+ 5 kuti ndikwaniritse lumbiro limene ndinalumbirira makolo anu kuti ndidzawapatsa dziko loyenda mkaka ndi uchi,+ ngati mmene zilili lero.’”’”
Pamenepo ine ndinayankha kuti: “Zikhale momwemo,* inu Yehova.”
6 Kenako Yehova anandiuza kuti: “Ulengeze mawu onsewa mʼmizinda ya Yuda ndi mʼmisewu ya Yerusalemu kuti: ‘Imvani mawu a pangano langa ndipo muchite zimene mawuwo akunena. 7 Inetu ndinkalangiza makolo anu pa tsiku limene ndinawatulutsa mʼdziko la Iguputo ndipo ndikupitiriza mpaka pano. Ndinkawalangiza mobwerezabwereza* kuti: “Muzimvera mawu anga.”+ 8 Koma iwo sanamvere kapena kutchera khutu. Mʼmalomwake aliyense wa iwo anapitiriza kuumitsa mtima wake ndi kuchita zofuna za mtima wake woipawo.+ Choncho ndinawalanga mogwirizana ndi mawu onse a mʼpangano langa limene ndinawalamula kuti azilitsatira koma iwo anakana kulitsatira.’”
9 Kenako Yehova anandiuza kuti: “Anthu a mu Yuda komanso okhala mu Yerusalemu akonza chiwembu choti andipandukire. 10 Iwo abwerera ku zolakwa za makolo awo akale amene anakana kumvera mawu anga.+ Iwonso atsatira milungu ina ndipo akuitumikira.+ A mʼnyumba ya Isiraeli ndi a mʼnyumba ya Yuda aphwanya pangano langa limene ndinachita ndi makolo awo.+ 11 Choncho Yehova wanena kuti, ‘Ndiwagwetsera tsoka+ limene sadzatha kulithawa. Akadzandiitana kuti ndiwathandize, sindidzawamvetsera.+ 12 Ndiyeno mizinda ya Yuda komanso anthu okhala mu Yerusalemu adzapita kukapempha thandizo kwa milungu imene akuifukizira nsembe.+ Koma milungu imeneyo sidzawapulumutsa pa nthawi ya tsoka lawo. 13 Chifukwa milungu yako, iwe Yuda, yafanana ndi mizinda yako kuchuluka kwake. Ndipo chinthu chochititsa manyazi mwachimangira* maguwa ansembe ochuluka mofanana ndi misewu ya mu Yerusalemu, maguwa ansembe oti muziperekerapo nsembe kwa Baala.’+
14 Koma iwe,* usawapempherere anthu awa. Usandilirire kuti ndiwathandize kapena kuwapempherera,+ chifukwa ine sindidzamvetsera pamene iwo akundiitana chifukwa cha tsoka limene lawagwera.
15 Nʼchifukwa chiyani anthu anga okondedwa akupezekabe mʼnyumba yanga
Pamene ambiri a iwo akuchita zinthu zoipa?
Kodi nyama yopatulika* idzawapulumutsa tsoka likadzawagwera?
Kodi iwo adzasangalala pa nthawi imeneyo?
16 Mʼmbuyomu Yehova ankakutchulani kuti mtengo wa maolivi wa masamba obiriwira,
Wokongola komanso wobala zipatso.
Koma pamveka phokoso lamphamvu ndipo mtengowo wauyatsa moto,
Ndipo adani athyola nthambi zake.
17 “Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, amene anakudzalani,+ wanena kuti tsoka lidzakugwerani chifukwa cha zoipa zimene a mʼnyumba ya Isiraeli ndi a mʼnyumba ya Yuda achita. Iwo andikhumudwitsa popereka nsembe kwa Baala.”+
18 Yehova anandiuza kuti ndidziwe,
Pa nthawiyo, inu Mulungu, munandionetsa zimene ankachita.
19 Ndinali ngati mwana wa nkhosa wamphongo womvera amene akupita kukaphedwa.
Sindinadziwe kuti andikonzera chiwembu nʼkunena kuti:+
“Tiyeni tiwononge mtengowu limodzi ndi zipatso zake,
Ndipo tiyeni timuchotse mʼdziko la anthu amoyo,
Kuti dzina lake lisadzakumbukiridwenso.”
20 Koma Yehova wa magulu ankhondo akumwamba amaweruza mwachilungamo.
Inu Mulungu, ndiloleni ndione mukuwapatsa chilango,
Chifukwa mlandu wanga ndausiya mʼmanja mwanu.
21 Choncho izi ndi zimene Yehova wanena zokhudza anthu a ku Anatoti+ amene akufuna kuchotsa moyo wako, ndipo akunena kuti: “Usanenere mʼdzina la Yehova+ ngati ukufuna kuti tisakuphe.” 22 Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti: “Ine ndidzawapatsa chilango. Anyamata adzafa ndi lupanga+ ndipo ana awo aamuna ndi aakazi adzafa ndi njala.+ 23 Sipadzapezeka ngakhale munthu mmodzi wotsala pakati pawo chifukwa ndidzabweretsa tsoka pa anthu a ku Anatoti,+ mʼchaka chimene ndidzawapatse chilango.”
12 Inu Yehova, ndikabweretsa dandaulo langa kwa inu,
Komanso ndikamalankhula ndi inu nkhani zokhudza chilungamo, mumasonyeza kuti ndinu wolungama.+
Koma nʼchifukwa chiyani anthu oipa, zinthu zikuwayendera bwino,+
Ndipo nʼchifukwa chiyani anthu amene amachita zachinyengo amakhala opanda nkhawa?
2 Munawadzala ndipo iwo anazika mizu.
Akula ndipo abala zipatso.
Amakutchulani pafupipafupi, koma mtima wawo uli kutali* kwambiri ndi inu.+
3 Koma inu Yehova, mukundidziwa bwino+ ndipo mumandiona.
Mwafufuza mtima wanga ndipo mwapeza kuti ndine wokhulupirika kwa inu.+
Apatuleni ngati nkhosa zimene zikukaphedwa,
Ndipo muwaike padera poyembekezera tsiku limene adzaphedwe.
4 Kodi dzikoli likhalabe lofota mpaka liti?
Kodi zomera zamʼmunda uliwonse zikhalabe zouma mpaka liti?+
Chifukwa cha zinthu zoipa zimene anthu amʼdzikoli akuchita,
Zilombo zakutchire ndi mbalame zawonongedwa.
Chifukwa anthuwo akuti: “Iye sakuona zimene zidzatichitikire.”
5 Ngati ukutopa pothamanga ndi anthu oyenda pansi,
Ndiye ungapikisane bwanji ndi mahatchi?+
Ukhoza kuona kuti ndiwe wotetezeka mʼdziko lamtendere,
Koma kodi udzatani ukadzakhala mʼnkhalango zowirira zamʼmphepete mwa Yorodano?
6 Chifukwa ngakhale abale ako enieni, anthu a mʼnyumba ya bambo ako,
Akuchitira zinthu zachinyengo.+
Iwo akunenera zinthu zoipa mofuula.
Usawakhulupirire,
Ngakhale atamalankhula zinthu zabwino kwa iwe.
7 “Nyumba yanga ndaisiya.+ Ndasiya cholowa changa.+
Wokondedwa wanga ndamupereka mʼmanja mwa adani ake.+
8 Cholowa changa chakhala ngati mkango kwa ine munkhalango.
Wokondedwa wanga wandibangulira.
Nʼchifukwa chake ndadana naye.
9 Cholowa changa chili ngati mbalame yanthenga zamitundu yosiyanasiyana imene imadya nyama.
Mbalame zina zodya nyama zaizungulira nʼkuiukira.+
Bwerani, sonkhanani pamodzi inu nyama zonse zamʼtchire,
Bwerani kuti mudzadye.+
Malo omwe ndi cholowa changa chosiririka awasandutsa bwinja moti palibe aliyense amene akukhalamo.
11 Cholowa changacho chasanduka chipululu,
Dziko lonse lakhala bwinja,
Koma palibe aliyense amene zikumukhudza.+
12 Anthu owononga adutsa mʼnjira zonse zodutsidwadutsidwa zamʼchipululu,
Chifukwa lupanga la Yehova likuwononga anthu kuchokera kumalekezero a dziko kukafika kumalekezero ena a dziko.+
Ndipo palibe munthu aliyense amene ali pamtendere.
13 Afesa tirigu koma akolola minga.+
Agwira ntchito yotopetsa koma osapeza phindu lililonse.
Iwo adzachita manyazi ndi zokolola zawo
Chifukwa mkwiyo waukulu wa Yehova udzawayakira.”
14 Yehova wanena kuti: “Anthu onse oipa amene ndinayandikana nawo amene akukhudza cholowa chimene ndinapatsa anthu anga Aisiraeli kuti chikhale chawo,+ ndikuwazula mʼdziko lawo+ ndipo ndidzazula nyumba ya Yuda pakati pawo. 15 Koma ndikadzawazula, ndidzawachitiranso chifundo moti ndidzabwezeretsa aliyense wa iwo pacholowa chake ndi pamalo ake.
16 Ndiyeno anthu a mitundu ina akadzayesetsa kuphunzira njira za anthu anga ndi kulumbira mʼdzina langa kuti, ‘Pali Yehova Mulungu wamoyo!’ ngati mmene iwo anaphunzitsira anthu anga kulumbira mʼdzina la Baala, anthu a mitundu inawo adzakhazikika pakati pa anthu anga. 17 Koma akadzakana kumvera, ine ndidzazulanso anthu a mtundu umenewo. Ndidzawazula nʼkuwawononga,” akutero Yehova.+
13 Yehova anandiuza kuti: “Pita ukagule lamba wansalu ndipo ukamumange mʼchiuno mwako, koma usakamuviike mʼmadzi.” 2 Choncho ndinakagula lambayo mogwirizana ndi mawu a Yehova ndipo ndinamumanga mʼchiuno mwanga. 3 Ndiyeno Yehova analankhulanso nane kachiwiri kuti: 4 “Tenga lamba wagula uja, amene wamumanga mʼchiuno ndipo unyamuke nʼkupita kumtsinje wa Firate. Kumeneko ukamubise mumngʼalu wamʼphanga.” 5 Choncho ndinapita nʼkukabisa lambayo pafupi ndi mtsinje wa Firate mogwirizana ndi zimene Yehova anandilamula.
6 Koma patapita masiku ambiri Yehova anandiuza kuti: “Nyamuka, pita kumtsinje wa Firate ndipo ukatenge lamba amene ndinakulamula kuti ukabise kumeneko.” 7 Choncho ndinapita kumtsinje wa Firate ndipo ndinakumba pamalo amene ndinabisapo lambayo nʼkumutenga. Koma ndinaona kuti anali atawonongeka moti sakanagwiranso ntchito iliyonse.
8 Kenako Yehova anandiuzanso kuti: 9 “Yehova wanena kuti, ‘Mofanana ndi lamba ameneyu, ndidzawononga kunyada kwa Yuda ndiponso kunyada kwakukulu kwa Yerusalemu.+ 10 Anthu oipawa, amene akukana kumvera mawu anga,+ amene mouma khosi amatsatira zofuna za mitima yawo+ ndipo akutsatira milungu ina, akuitumikira komanso kuigwadira, adzakhala ngati lamba ameneyu amene sangagwirenso ntchito iliyonse.’ 11 ‘Mofanana ndi mmene lamba amagwirira mʼchiuno mwa munthu, ine ndinachititsa nyumba yonse ya Isiraeli ndi nyumba yonse ya Yuda kundimamatira,’ akutero Yehova. ‘Ndinachita zimenezi kuti iwo akhale anthu anga,+ atchukitse dzina langa,+ anditamande ndi kukhala chinthu changa chokongola. Koma iwo sanandimvere.’+
12 Ukawauzenso uthenga wakuti, ‘Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti: “Mtsuko uliwonse waukulu amadzazamo vinyo.”’ Ukakawauza zimenezi akakufunsa kuti, ‘Kodi ife sitikudziwa kuti mtsuko uliwonse waukulu amadzazamo vinyo?’ 13 Kenako ukawauze kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Inetu ndikuledzeretsa anthu onse amʼdzikoli,+ mafumu amene akukhala pampando wachifumu wa Davide, ansembe, aneneri ndi anthu onse amene amakhala mu Yerusalemu. 14 Ndipo ndidzawombanitsa munthu ndi mnzake, abambo chimodzimodzinso ana,” akutero Yehova.+ “Sindidzawakomera mtima, kuwamvera chisoni kapena kuwachitira chifundo. Palibe chimene chidzandilepheretse kuti ndiwawononge.”’+
15 Tamverani ndipo mutchere khutu.
Musadzikweze chifukwa Yehova ndi amene wanena zimenezi.
16 Perekani ulemerero kwa Yehova Mulungu wanu
Asanabweretse mdima,
Komanso mapazi anu asanapunthwe pamapiri madzulo dzuwa litalowa.
Mudzayembekezera kuwala,
Koma iye adzabweretsa mdima waukulu,
Ndipo adzachititsa kuti mdimawo ukhale wandiweyani.+
17 Ndipo mukakana kumvera,
Ndidzalira mobisa chifukwa cha kunyada kwanu.
Ndidzagwetsa misozi yambiri ndipo misozi idzatsika kuchokera mʼmaso mwanga+
Chifukwa nkhosa za Yehova+ zagwidwa nʼkutengedwa kupita kudziko lina.
18 Uza mfumu ndi mayi a mfumu kuti,+ ‘Khalani pamalo apansi,
Chifukwa chisoti chanu chaulemerero chidzagwera pansi kuchoka kumutu kwanu.’
19 Mizinda yakumʼmwera yatsekedwa* ndipo palibe amene angaitsegule.
Anthu onse a mu Yuda atengedwa kupita ku ukapolo. Onse atengedwa kupita ku ukapolo popanda wotsala.+
20 Kweza maso ako kuti uone anthu amene akubwera kuchokera kumpoto.+
Kodi ziweto zimene anakupatsa, nkhosa zako zokongola zija zili kuti?+
21 Kodi udzanena chiyani chilango chako chikadzabwera
Kuchokera kwa anzako apamtima, amene unkagwirizana nawo kuchokera pa chiyambi?+
Kodi sudzamva zowawa za pobereka ngati za mkazi amene akubereka mwana?+
22 Ndipo ukadzanena mumtima mwako kuti, ‘Nʼchifukwa chiyani zinthu zimenezi zandigwera?’+
Udzadziwe kuti wavulidwa siketi yako chifukwa cha kuchuluka kwa machimo ako+
Ndipo zidendene zako zazunzidwa.
23 “Kodi Mkusi* angasinthe khungu lake, kapena kodi kambuku angasinthe mawanga ake?+
Ngati angathe kuchita zimenezi, ndiye kuti inunso amene munaphunzitsidwa kuchita zinthu zoipa,
Mungathe kuchita zinthu zabwino.
24 Choncho ndidzakumwazani ngati mapesi amene akuuluzidwa ndi mphepo yochokera mʼchipululu.+
25 Zimenezi ndi zimene zidzakuchitikire. Limeneli ndi gawo limene ndakupatsa,” akutero Yehova,
“Chifukwa chakuti wandiiwala+ ndipo ukukhulupirira zinthu zabodza.+
26 Choncho ndidzakuvula siketi yako nʼkukuphimba nayo kumaso,
Ndipo anthu adzaona maliseche ako.+
27 Chigololo chimene ukuchita,+ kumemesa* kwako,
Khalidwe lako lonyansa* la uhule, zonsezi zidzaonekera.
Ndaona khalidwe lako lonyansa+
Mʼmapiri komanso kuthengo.
Tsoka kwa iwe Yerusalemu!
Kodi ukhalabe wodetsedwa mpaka liti?”+
14 Mawu amene Yehova anauza Yeremiya pa nkhani ya chilala ndi awa:+
2 Yuda akulira maliro+ ndipo mageti ake agwa.
Agwa pansi nʼkumalira momvetsa chisoni,
Ndipo anthu a ku Yerusalemu akulira.
3 Anthu awo olemekezeka amatuma antchito awo kuti akatunge madzi.
Antchitowo amapita kuzitsime koma sapezako madzi.
Amabwerako ndi ziwiya zopanda kanthu.
Iwo achita manyazi ndipo akhumudwa,
Moti aphimba mitu yawo.
4 Alimi ataya mtima ndipo aphimba mitu yawo
Chifukwa chakuti mʼdzikomo simunagwe mvula+
Ndipo nthaka yangʼambikangʼambika.
5 Ngakhale mbawala yaikazi yasiya mwana wake wobadwa kumene mʼthengo
Chifukwa kulibe msipu.
6 Abulu amʼtchire angoima mʼmapiri opanda kanthu.
Akupuma mwawefuwefu ngati mimbulu.
Maso awo achita mdima chifukwa kulibe msipu.+
7 Ngakhale kuti machimo athu akuchitira umboni kuti ndife olakwa,
Inu Yehova, chitanipo kanthu chifukwa cha dzina lanu.+
Chifukwa zochita zathu zosonyeza kusakhulupirika nʼzambiri,+
Ndipo takuchimwirani.
8 Inu chiyembekezo cha Isiraeli, Mpulumutsi wake+ pa nthawi yamavuto,
Nʼchifukwa chiyani mukukhala ngati mlendo mʼdzikoli?
Nʼchifukwa chiyani mukukhala ngati munthu wapaulendo amene waima kuti agone usiku umodzi wokha?
9 Nʼchifukwa chiyani mukukhala ngati munthu wothedwa nzeru,
Ndiponso ngati munthu wamphamvu amene sangathe kupulumutsa anthu ake?
Musatisiye.
10 Ponena za anthu awa Yehova wanena kuti: “Iwo amakonda kumangoyendayenda+ ndipo samatha kudziletsa kuti asamayendeyende.+ Choncho Yehova sakusangalala nawo.+ Tsopano iye akumbukira zolakwa zawo ndipo awalanga chifukwa cha machimo awo.”+
11 Kenako Yehova anandiuza kuti: “Usapempherere anthu awa kuti zinthu ziwayendere bwino.+ 12 Akamasala kudya, ine sindimvetsera kuchonderera kwawo.+ Akamapereka nsembe zopsereza zathunthu ndi nsembe zambewu, ine sindisangalala nazo+ ndipo ndiwawononga ndi lupanga, njala yaikulu ndiponso mliri.”*+
13 Nditamva zimenezi ndinanena kuti: “Mayo ine! Inu Yehova Ambuye Wamkulu Koposa. Aneneri akuuza anthuwo kuti, ‘Simudzawonongedwa ndi lupanga ndipo njala yaikulu sidzakugwerani, koma Mulungu adzakupatsani mtendere weniweni mʼmalo ano.’”+
14 Ndiyeno Yehova anandiyankha kuti: “Aneneriwo akulosera zinthu zabodza mʼdzina langa.+ Ine sindinawatume, kuwalamula kapena kulankhula nawo.+ Maulosi amene akukuuzaniwo ndi masomphenya abodza, maulosi opanda pake ndi chinyengo chamumtima mwawo.+ 15 Choncho Yehova wanena kuti: ‘Ponena za aneneri amene akulosera mʼdzina langa ngakhale kuti sindinawatume, amenenso akunena kuti lupanga kapena njala sizidzafika mʼdziko lino, ine ndikuti aneneri amenewo adzaphedwa ndi lupanga ndiponso njala yaikulu.+ 16 Anthu amene akuwauza maulosi awowo, adzafa ndi njala komanso lupanga ndipo mitembo yawo idzatayidwa mʼmisewu ya Yerusalemu. Sipadzakhala wowaika mʼmanda,+ iwowo, akazi awo, ana awo aamuna kapena ana awo aakazi chifukwa ndidzawatsanulira tsoka limene akuyenera kulandira.’+
17 Anthu awa uwauze kuti,
‘Maso anga atulutse misozi usiku ndi masana ndipo asasiye,+
Chifukwa mwana wamkazi wa anthu anga, yemwe ndi namwali, waphwanyidwa kotheratu+
Ndipo ali ndi bala lalikulu kwambiri.
18 Ndikapita kunja kwa mzinda,
Ndikuona anthu ophedwa ndi lupanga.+
Ndipo ndikalowa mumzinda,+
Ndikuona matenda obwera chifukwa cha njala.
Aneneri komanso ansembe, onse apita kudziko lachilendo limene sakulidziwa.’”+
19 Kodi Yuda mwamukaniratu, kapena kodi mukunyansidwa ndi Ziyoni?+
Nʼchifukwa chiyani mwatilanga chonchi moti sitingathenso kuchira?+
Timayembekezera mtendere, koma palibe chabwino chilichonse chimene chachitika.
Timayembekezera kuchiritsidwa, koma tikungoona zinthu zochititsa mantha.+
20 Inu Yehova, ife tikuvomereza zinthu zoipa zimene tachita
Komanso kulakwa kwa makolo athu,
Chifukwa takuchimwirani.+
21 Koma chifukwa cha dzina lanu, musatikane.+
Musachititse manyazi mpando wanu wachifumu waulemerero.
Kumbukirani pangano limene munachita ndi ife ndipo musaliphwanye.+
22 Kodi pa mafano opanda pake a mitundu ya anthu pali fano lililonse limene lingagwetse mvula?
Kapena kodi kumwamba pakokha kungagwetse mvula yamvumbi?
Kodi si inu nokha, Yehova Mulungu wathu, amene mumachititsa zimenezi?+
Chiyembekezo chathu chili mwa inu
Chifukwa inu nokha ndi amene mumachita zonsezi.
15 Kenako Yehova anandiuza kuti: “Ngakhale Mose ndi Samueli akanaima pamaso panga,+ anthu awa sindikanawakomera mtima. Achotse pamaso panga. Asiye apite. 2 Ndiyeno akakufunsa kuti, ‘Tipite kuti?’ uwayankhe kuti, ‘Yehova wanena kuti:
“Amene akuyenera kufa ndi mliri afe ndi mliri!
Amene akuyenera kufa ndi lupanga afe ndi lupanga!+
Amene akuyenera kufa ndi njala yaikulu afe ndi njala yaikulu!
Amene akuyenera kutengedwa kupita ku ukapolo atengedwe kupita ku ukapolo!”’+
3 “‘Ndidzawabweretsera masoka okwanira 4,’*+ akutero Yehova. ‘Ndidzawatumizira lupanga kuti liwaphe, agalu kuti akoke mitembo yawo, mbalame zamumlengalenga komanso zilombo zakutchire kuti ziwadye ndi kuwawononga.+ 4 Ndidzawasandutsa chinthu chochititsa mantha kwa maufumu onse apadziko lapansi,+ chifukwa cha zimene Manase mwana wa Hezekiya, mfumu ya Yuda, anachita mu Yerusalemu.+
5 Ndi ndani adzakusonyeze chifundo, iwe Yerusalemu?
Ndi ndani adzakumvere chisoni,
Ndipo ndi ndani adzapatuke kuti afunse za moyo wako?’
6 ‘Iwe wandisiya,’ akutero Yehova.+
‘Ukupitiriza kubwerera nʼkundisiya.*+
Choncho ndidzakutambasulira dzanja langa nʼkukuwononga.+
Ndatopa ndi kukumvera chisoni.*
7 Ndidzawapeta kuti auluzike ndi mphepo pamageti amʼdzikoli.
Ndidzawaphera ana awo.+
Ndidzawononga anthu anga,
Chifukwa akukana kusiya kuyenda mʼnjira zawo.+
8 Akazi awo amasiye adzachuluka kwambiri pamaso panga kuposa mchenga wakunyanja.
Ndidzawabweretsera wowononga masana, adzawononga amayi ndi anyamata.
Ndidzawachititsa kuti asokonezeke komanso kugwidwa ndi mantha mwadzidzidzi.
9 Mkazi amene wabereka ana 7 wafooka,
Ndipo akupuma movutikira.
Kwa iye dzuwa lalowa masanasana,
Iye wachita manyazi ndipo wathedwa nzeru.’*
Ndipo anthu awo otsala omwe ndi ochepa
Ndidzawapereka kwa adani awo kuti awaphe ndi lupanga,’ akutero Yehova.”+
10 Tsoka ine, chifukwa inu mayi anga munabereka ine,+
Munthu amene nthawi zonse ndimakangana ndi dziko lonse komanso kulimbana nalo.
Sindinakongole kanthu kapena kukongoza wina aliyense,
Koma anthu onse akunditemberera.
11 Yehova anandiuza kuti: “Ndithu ndidzakuchitira zinthu zabwino.
Ndithu ndidzakuthandiza pa nthawi ya tsoka,
Ndidzakuthandiza pa nthawi yamavuto.
12 Kodi munthu angathe kuthyolathyola chitsulo?
Kodi angathe kuthyolathyola chitsulo chakumpoto ndi kopa?*
13 Chuma chanu komanso zinthu zanu zamtengo wapatali ndidzazipereka kwa adani anu kuti azitenge.+
Adzazitenga popanda malipiro chifukwa cha machimo anu onse amene munachita mʼdziko lanu lonse.
14 Ndidzazipereka kwa adani anu
Kuti azitenge nʼkupita nazo kudziko limene simukulidziwa.+
Chifukwa mkwiyo wanga wayatsa moto,
Ndipo motowo ukukuyakirani.”+
15 Inu Yehova mukudziwa bwino mavuto anga.
Ndikumbukireni ndi kundiyangʼana.
Mundibwezerere anthu amene akundizunza.+
Musalole kuti ndiwonongeke chifukwa chakuti mukuwalezera mtima.
Dziwani kuti ndikunyozedwa chifukwa cha inu.+
16 Mawu anu anandipeza ndipo ndinawadya.+
Mawu anu anakondweretsa komanso kusangalatsa mtima wanga,
Chifukwa ine ndimatchedwa ndi dzina lanu, inu Yehova Mulungu wa magulu ankhondo akumwamba.
17 Sindikhala pansi ndi gulu la anthu okonda zosangalatsa nʼkumasangalala nawo.+
18 Nʼchifukwa chiyani ululu wanga sukutha ndiponso bala langa silikupola?
Balali silikumva mankhwala.
Kodi mukhala ngati chitsime chosathandiza
Chimene munthu sangachidalire?
19 Choncho Yehova wanena kuti:
“Ukabwerera, ine ndidzakukonda,
Ndipo udzapitiriza kunditumikira.*
Ukasiyanitsa zinthu zamtengo wapatali ndi zinthu zopanda phindu,
Udzakhala ngati pakamwa panga.*
Anthuwo adzayenera kubwera kwa iwe,
Koma iwe sudzapita kwa iwo.”
20 “Ndakuchititsa kuti ukhale ngati mpanda wakopa wolimba kwambiri kwa anthu awa.+
Iwo adzamenyana nawe ndithu,
Koma sadzakugonjetsa,+
Chifukwa ine ndili ndi iwe kuti ndikupulumutse komanso kukulanditsa,” akutero Yehova.
21 “Ndidzakulanditsa mʼmanja mwa anthu oipa
Ndipo ndidzakuwombola mʼmanja mwa anthu ankhanza.”
16 Ndiyeno Yehova anandiuzanso kuti: 2 “Usakwatire ndipo usakhale ndi ana aamuna kapena ana aakazi mʼmalo ano. 3 Ponena za ana aamuna ndi ana aakazi amene adzabadwe mʼmalo ano, komanso ponena za amayi ndi abambo amene adzabereke anawo mʼdzikoli, Yehova akuti: 4 ‘Iwo adzafa ndi matenda oopsa+ koma palibe amene adzalire maliro awo kapena kuwaika mʼmanda. Iwo adzakhala ngati manyowa panthaka.+ Adzafa ndi lupanga ndiponso njala.+ Mitembo yawo idzakhala chakudya cha mbalame zamumlengalenga ndi zilombo zakutchire.’
5 Yehova wanena kuti,
‘Usalowe mʼnyumba imene olira maliro akuchitiramo phwando,
Ndipo usapite kukalira nawo maliro kapena kukapepesa.+
Chifukwa anthu awa ndawachotsera mtendere wanga,
Komanso chikondi changa chokhulupirika ndi chifundo changa,’ akutero Yehova.+
6 ‘Anthu amʼdzikoli adzafa, kaya ndi olemekezeka kapena onyozeka.
Sadzaikidwa mʼmanda,
Palibe aliyense amene adzalire maliro awo,
Kapena kudzichekacheka komanso kumeta mpala chifukwa cha iwo.*
7 Palibe amene adzapereke chakudya kwa anthu amene akulira maliro,
Kuti awatonthoze chifukwa cha maliro amene awagwera,
Komanso palibe amene adzawapatse kapu ya vinyo kuti awatonthoze
Kuti amwe chifukwa cha imfa ya bambo awo kapena mayi awo.
8 Ndipo usadzalowe mʼnyumba yaphwando
Kuti ukhale nawo pansi nʼkumadya ndi kumwa.’
9 Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti, ‘Mʼmasiku anu, ndidzathetsa phokoso lachikondwerero, phokoso lachisangalalo, mawu a mkwati ndi mawu a mkwatibwi mʼmalo ano, inuyo mukuona.’+
10 Ukadzauza anthu awa mawu onsewa, iwo adzakufunsa kuti, ‘Nʼchifukwa chiyani Yehova wanena kuti adzatigwetsera tsoka lalikulu limeneli? Kodi talakwa chiyani ndipo tamuchimwira chiyani Yehova Mulungu wathu?’+ 11 Udzawayankhe kuti, ‘“Chifukwa chakuti makolo anu anandisiya,”+ akutero Yehova, “ndipo anapitiriza kutsatira milungu ina, kuitumikira ndi kuigwadira.+ Koma ine anandisiya ndipo sanasunge malamulo anga.+ 12 Ndipo inu mwachita zinthu zoipa kwambiri kuposa makolo anu.+ Aliyense wa inu akupitiriza kuumitsa khosi nʼkumatsatira mtima wake woipawo mʼmalo mondimvera.+ 13 Choncho ndidzakuchotsani mʼdziko lino nʼkukupititsani kudziko limene inu kapena makolo anu sankalidziwa.+ Kumeneko mukatumikira milungu ina masana ndi usiku+ chifukwa sindidzakuchitirani chifundo.”’
14 ‘Komabe masiku akubwera,’ akutero Yehova, ‘pamene sadzalumbiranso kuti: “Pali Yehova Mulungu wamoyo amene anatulutsa Aisiraeli mʼdziko la Iguputo!”+ 15 Koma adzalumbira kuti: “Pali Yehova Mulungu wamoyo amene anatulutsa Aisiraeli mʼdziko lakumpoto komanso kuchokera mʼmayiko onse kumene anawabalalitsira!” Ineyo ndidzawabwezera kudziko lawo limene ndinapatsa makolo awo.’+
16 ‘Ine ndikuitana asodzi ambiri,’ akutero Yehova,
‘Ndipo adzawawedza.
Kenako ndidzaitana anthu ambiri osaka nyama,
Ndipo adzawasaka mʼphiri lililonse, pachitunda chilichonse,
Komanso mʼmapanga a mʼmatanthwe.
17 Chifukwa maso anga akuona chilichonse chimene akuchita.*
Anthuwo sanabisike kwa ine,
Ndipo zolakwa zawo sizinabisike pamaso panga.
18 Choyamba ndidzawabwezera zolakwa zawo zonse ndi machimo awo onse,+
Chifukwa aipitsa dziko langa ndi zifaniziro zopanda moyo za mafano* awo onyansa
Ndipo adzaza cholowa changa ndi zinthu zawo zonyansa.’”+
19 Inu Yehova, ndinu mphamvu yanga komanso malo anga achitetezo,
Malo anga othawirako pa tsiku lamavuto,+
Mitundu ya anthu idzabwera kwa inu kuchokera kumalekezero a dziko lapansi,
Ndipo idzati: “Makolo athu analandira mafano monga cholowa chawo,
Analandira zinthu zachabechabe komanso zosapindulitsa.”+
20 Kodi munthu angapange milungu?
Zimene munthu amapangazo si milungu ayi.+
21 “Choncho ine ndiwaphunzitsa.
Pa nthawi ino ndiwachititsa kuti adziwe mphamvu ndi nyonga zanga,
Ndipo adziwa kuti dzina langa ndine Yehova.”
17 “Tchimo la Yuda lalembedwa ndi chitsulo chogobera.
Lalembedwa ndi cholembera cha dayamondi mʼmitima yawo
Ndi panyanga za maguwa awo ansembe.
2 Pamene ana awo aamuna akumbukira maguwa awo ansembe ndi mizati yawo yopatulika*+
Pafupi ndi mtengo wamasamba ambiri obiriwira, pamwamba pa zitunda zazitali,+
3 Pamapiri amene ali mʼmadera akumidzi.
Katundu wanu ndi chuma chanu chonse ndidzazipereka kwa adani anu kuti azitenge.+
Ndidzapereka malo anu okwezeka chifukwa cha tchimo limene lachitika mʼmadera anu onse.+
4 Mwa kufuna kwanu, mudzataya cholowa chimene ndinakupatsani.+
Ndipo ndidzakuchititsani kuti mutumikire adani anu mʼdziko limene simukulidziwa.+
Moto wake udzayakabe mpaka kalekale.”
5 Yehova wanena kuti:
“Wotembereredwa ndi munthu amene amakhulupirira munthu mnzake.+
Wotembereredwa ndi munthu amene amadalira mphamvu za munthu,+
Komanso amene mtima wake wapatuka kuchoka kwa Yehova.
6 Iye adzakhala ngati mtengo umene uli pawokhawokha mʼchipululu.
Zabwino zikadzafika sadzatha kuziona,
Koma adzakhala mʼmalo ouma amʼchipululu,
Mʼdziko la nthaka yamchere, kumene sikungakhale munthu aliyense.
7 Munthu amene amakhulupirira Yehova komanso amene amadalira Yehova,
Ndi amene amadalitsidwa.+
8 Iye adzakhala ngati mtengo wodzalidwa mʼmphepete mwa madzi,
Umene mizu yake imakafika mumtsinje.
Ngakhale dzuwa litawotcha kwambiri iye sadzamva kutentha,
Koma nthawi zonse masamba ake adzakhala obiriwira.+
Ndipo pa nthawi ya chilala sadzada nkhawa,
Kapena kusiya kubala zipatso.
9 Mtima ndi wopusitsa* kwambiri kuposa chinthu chilichonse ndipo ungathe kuchita china chilichonse choipa.*+
Ndi ndani angaudziwe?
10 Ine Yehova ndimafufuza mtima,+
Ndimafufuza maganizo a mkati mwa mtima wa munthu,*
Kuti munthu aliyense ndimuchitire zinthu mogwirizana ndi zochita zake,
Komanso mogwirizana ndi zipatso za ntchito zake.+
11 Munthu amene amapeza chuma mwachinyengo,*+
Ali ngati nkhwali imene imasonkhanitsa mazira amene sinaikire.
Chuma chakecho chidzatha asanakwanitse hafu ya zaka za moyo wake,
Ndipo pamapeto pake adzadziwika kuti ndi wopusa.”
12 Mpando waulemerero wa Mulungu ndi wokwezeka kuyambira pa chiyambi,
Ndipo ndi malo athu opatulika.+
13 Inu Yehova, chiyembekezo cha Isiraeli,
Onse amene akukusiyani adzachita manyazi.
Anthu onse okupandukirani mayina awo adzalembedwa pafumbi,+
Chifukwa asiya Yehova, amene ndi kasupe wa madzi opatsa moyo.+
14 Ndichiritseni inu Yehova, ndipo ndidzachiradi.
Ndipulumutseni ndipo ndidzapulumukadi,+
Chifukwa ine ndimatamanda inu.
15 Taonani! Ena akunena kuti:
“Nʼchifukwa chiyani mawu a Yehova sanakwaniritsidwebe?+
Tsopanotu akwaniritsidwe.”
16 Koma ine sindinaleke kukutsatirani monga mʼbusa wanu,
Kapena kulakalaka tsiku latsoka.
Inu Mulungu, mukudziwa bwino zimene pakamwa panga panalankhula,
Chifukwa ndinalankhula pamaso panu.
17 Musakhale chinthu chochititsa mantha kwa ine.
Inu ndinu malo anga othawirako pa tsiku la tsoka.
18 Anthu amene amandizunza achite manyazi,+
Koma musalole kuti ineyo ndichite manyazi.
Anthuwo agwidwe ndi mantha aakulu,
Koma musalole kuti ine ndigwidwe ndi mantha aakulu.
19 Yehova wandiuza kuti: “Pita ukaime pageti la ana a anthu, pamene mafumu a Yuda amalowera ndi kutulukira komanso ukaime pamageti onse a mu Yerusalemu.+ 20 Ndipo ukawauze kuti, ‘Tamverani mawu a Yehova, inu mafumu a Yuda ndi anthu nonse amene mukukhala mu Yuda komanso inu nonse amene mukukhala mu Yerusalemu, amene mumalowera pamageti awa. 21 Yehova wanena kuti: “Samalani kuti musanyamule katundu aliyense kapena kulowa naye pamageti a Yerusalemu pa tsiku la Sabata.+ 22 Musamatulutse katundu aliyense mʼnyumba zanu pa tsiku la Sabata ndipo musamagwire ntchito iliyonse.+ Muziona kuti tsiku la Sabata ndi lopatulika mogwirizana ndi zimene ndinalamula makolo anu.+ 23 Koma iwo sanamvere kapena kutchera khutu ndipo anaumitsa mtima wawo nʼkukana* kundimvera komanso kulandira malangizo.”’+
24 ‘“Koma mukandimvera mosamala,” akutero Yehova, “ndipo mukapanda kulowa ndi katundu pamageti a mzindawu pa tsiku la Sabata komanso mukamaona kuti tsiku la Sabata ndi lopatulika popewa kugwira ntchito iliyonse pa tsikuli,+ 25 mafumu ndi akalonga amene amakhala pampando wachifumu wa Davide+ nawonso adzalowa pamageti a mzindawu. Adzalowa atakwera magaleta ndi mahatchi, mafumuwo ndi akalonga awo, anthu a mu Yuda komanso anthu amene akukhala mu Yerusalemu+ ndipo mumzindawu mudzakhala anthu mpaka kalekale. 26 Anthu adzabwera kuchokera mʼmizinda ya Yuda, mʼmadera ozungulira Yerusalemu, mʼdziko la Benjamini,+ kuchigwa,+ mʼdera lamapiri komanso kuchokera ku Negebu.* Iwo adzabweretsa kunyumba ya Yehova nsembe zopsereza zathunthu,+ nsembe zina,+ nsembe zambewu,+ lubani* ndi nsembe zoyamikira.+
27 Koma ngati simudzandimvera nʼkusiya kuona kuti tsiku la Sabata ndi lopatulika komanso mukadzanyamula katundu nʼkulowa naye pamageti a Yerusalemu pa tsiku la Sabata, ine ndidzawotcha ndi moto mageti a mzindawu. Motowo udzawotcha nsanja zokhala ndi mipanda yolimba za Yerusalemu+ ndipo sudzazimitsidwa.”’”+
18 Mawu amene Yehova anauza Yeremiya ndi awa: 2 “Nyamuka, upite kunyumba ya woumba mbiya+ ndipo ndikakuuza mawu anga kumeneko.”
3 Choncho ndinapita kunyumba ya woumba mbiya, ndipo ndinamupeza akugwira ntchito yake pamalo oumbira mbiya. 4 Koma chiwiya chimene woumba mbiyayo ankapanga ndi dongo chinawonongeka mʼmanja mwake. Choncho iye anasintha nʼkupanga chiwiya china ndi dongo lomwelo, malinga ndi zimene anaona kuti nʼzabwino.
5 Kenako Yehova anandiuza kuti: 6 “‘Inu a nyumba ya Isiraeli, kodi sindingakuchiteni zofanana ndi zimene woumba mbiyayu anachita?’ akutero Yehova. ‘Tamverani! Mofanana ndi dongo limene lili mʼmanja mwa woumba mbiya, ndi mmene inunso mulili kwa ine, inu nyumba ya Isiraeli.+ 7 Nthawi iliyonse imene ndinganene kuti ndizula, kugwetsa ndi kuwononga mtundu uliwonse wa anthu kapena ufumu,+ 8 ndiyeno mtundu wa anthuwo nʼkusiya zoipa zimene ndinawadzudzula nazo, inenso ndidzasintha maganizo anga okhudza tsoka limene ndimafuna kuwagwetsera.+ 9 Koma nthawi iliyonse imene ndinganene kuti ndimanga ndi kudzala mtundu wa anthu kapena ufumu, 10 ndiyeno mtundu wa anthuwo nʼkumachita zoipa pamaso panga ndiponso osamvera mawu anga, inenso ndidzasintha maganizo anga okhudza zinthu zabwino zimene ndinkafuna kuwachitira.’
11 Tsopano uza anthu a mu Yuda ndi anthu okhala mu Yerusalemu kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Inetu ndikukukonzerani tsoka ndipo ndikuganizira njira yokulangirani. Chonde, bwererani nʼkusiya njira zanu zoipa. Sinthani zochita zanu ndi makhalidwe anu.”’”+
12 Koma iwo anati: “Zimenezo ayi!+ Ife titsatira maganizo athu, ndipo aliyense wa ife adzachita zinthu mouma khosi, mogwirizana ndi mtima wake woipa.”+
13 Choncho Yehova wanena kuti:
“Funsafunsani pakati pa mitundu ya anthu.
Ndi ndani amene anamvapo zoterezi?
Namwali wa Isiraeli wachita chinthu choopsa kwambiri.+
14 Kodi sinowo wamʼmapiri a ku Lebanoni amasungunuka* nʼkuchoka pamiyala yake?
Kapena kodi madzi ozizira bwino amene akuyenda kuchokera kutali adzauma?
15 Koma anthu anga andiiwala.+
Chifukwa akupereka nsembe* kwa chinthu chopanda pake+
Ndipo akuchititsa kuti anthu amene akuyenda mʼnjira zawo, mʼnjira zakale, apunthwe,+
Akuwachititsa kuti ayende mʼnjira zolakwika zomwe ndi zokumbikakumbika.*
16 Choncho dziko lawo lidzakhala chinthu chochititsa mantha+
Komanso chimene anthu azidzachiimbira mluzu mpaka kalekale.+
Aliyense wodutsa pafupi ndi dzikoli adzaliyangʼanitsitsa mwamantha ndipo adzapukusa mutu wake.+
17 Ndidzawamwaza pamaso pa adani awo ngati mmene mphepo yochokera kumʼmawa imamwazira fumbi.
Sindidzawaonetsa nkhope yanga, koma ndidzawafulatira pa tsiku la tsoka lawo.”+
18 Iwo ananena kuti: “Tabwerani, tiyeni timukonzere chiwembu Yeremiya,+ chifukwa ansembe adzapitiriza kutiphunzitsa chilamulo.* Anthu athu anzeru sadzasiya kutipatsa malangizo ndipo aneneri adzapitiriza kutiuza mawu a Mulungu. Bwerani, tiyeni titsutsane naye* ndipo tisamvere zimene akunena.”
19 Ndimvereni, inu Yehova,
Ndipo imvani zimene adani anga akunena.
20 Kodi akuyenera kubwezera zinthu zoipa pa zinthu zabwino?
Iwo akumba dzenje kuti achotse moyo wanga.+
Kumbukirani kuti ndinkaima pamaso panu nʼkumalankhula zabwino zokhudza anthu amenewa,
Kuti muwachotsere mkwiyo wanu.
21 Choncho lolani kuti ana awo afe ndi njala,
Komanso aphedwe ndi lupanga.+
Akazi awo akhale amasiye ndipo ana a akaziwo afe.+
Amuna awo afe ndi mliri woopsa
Ndipo anyamata awo aphedwe ndi lupanga pankhondo.+
22 Mʼnyumba zawo mumveke kulira
Mukawabweretsera magulu achifwamba mwadzidzidzi.
Chifukwa akumba dzenje kuti andigwire
Ndipo atchera misampha kuti akole mapazi anga.+
23 Koma inu Yehova,
Mukudziwa bwino ziwembu zawo zonse zimene andikonzera kuti andiphe.+
Musawakhululukire cholakwa chawo,
Ndipo musafafanize tchimo lawo pamaso panu.
19 Yehova wanena kuti: “Pita, ukagule botolo ladothi kwa woumba mbiya.+ Utenge ena mwa atsogoleri a anthu ndi ena mwa akuluakulu a ansembe, 2 nʼkupita ku Chigwa cha Mwana wa Hinomu,+ pakhomo la Geti la Mapale. Kumeneko ukanene mawu onse amene ndikuuze. 3 Ukawauze kuti, ‘Tamverani mawu a Yehova inu mafumu a Yuda ndi inu anthu amene mukukhala mu Yerusalemu. Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti:
‘“Ine ndatsala pangʼono kubweretsa tsoka pamalo ano ndipo aliyense akadzamva za tsoka limeneli, mʼmakutu mwake mudzachita phokoso. 4 Ndidzachita zimenezi chifukwa iwo andisiya+ ndiponso achititsa kuti malo ano ndisawazindikire.+ Pamalo ano iwo akupereka nsembe kwa milungu ina, imene iwowo, makolo awo komanso mafumu a Yuda sankaidziwa ndipo adzaza malo ano ndi magazi a anthu osalakwa.+ 5 Iwo amangira Baala malo okwera kuti aziwotcha pamoto ana awo aamuna ngati nsembe zopsereza zathunthu zoperekedwa kwa Baala.+ Ine sindinawalamule zimenezi kapena kuzitchula ndipo sindinaziganizirepo mumtima mwanga.+
6 Choncho taonani! masiku akubwera,” akutero Yehova, “pamene sadzatchulanso malowo kuti Tofeti kapena Chigwa cha Mwana wa Hinomu, koma adzawatchula kuti Chigwa Chopherako Anthu.+ 7 Ndidzasokoneza zolinga za Yuda ndi za Yerusalemu mʼmalo ano, ndipo ndidzachititsa kuti aphedwe ndi lupanga la adani awo komanso ndi anthu amene akufunafuna moyo wawo. Mitembo yawo ndidzaipereka kwa mbalame zamumlengalenga ndi zilombo zakutchire kuti ikhale chakudya chawo.+ 8 Mzindawu ndidzausandutsa chinthu chochititsa mantha komanso chimene anthu azidzachiimbira mluzu. Aliyense wodutsa pafupi ndi mzindawo adzauyangʼanitsitsa mwamantha ndipo adzauimbira mluzu chifukwa cha miliri yake yonse.+ 9 Ndidzawachititsa kudya mnofu wa ana awo aamuna ndi ana awo aakazi. Aliyense adzadya mnzake chifukwa adani adzawazungulira komanso chifukwa chosowa mtengo wogwira. Izi zidzachitika pamene adani awo ndiponso anthu amene akufuna moyo wawo adzawapanikize.”’+
10 Kenako ukaswe botololo pamaso pa amuna amene akupita nawe, 11 ndiyeno ukawauze kuti, ‘Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti: “Mofanana ndi zimenezi, ndidzaswa anthu awa ndi mzinda uwu ngati mmene munthu amaswera botolo lopangidwa ndi woumba mbiya moti silingathe kukonzedwanso. Iwo adzaika maliro ku Tofeti mpaka sipadzapezekanso malo oika maliro kumeneko.”’+
12 ‘Izi ndi zimene ndidzachite ndi malo awa ndiponso ndi anthu onse amene akukhala mmenemu kuti mzindawu ukhale ngati Tofeti,’ akutero Yehova. 13 ‘Nyumba za mu Yerusalemu ndi nyumba za mafumu a Yuda zidzakhala zodetsedwa ngati malo ano a Tofeti.+ Zimenezi ndi nyumba zonse zimene pamadenga ake ankaperekapo nsembe kwa gulu lonse la zinthu zakuthambo+ ndi kuthirapo nsembe zachakumwa kwa milungu ina.’”+
14 Yeremiya atabwerako ku Tofeti kumene Yehova anamutuma kuti akalosere, anakaima mʼbwalo la nyumba ya Yehova nʼkuuza anthu onse kuti: 15 “Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti, ‘Ine ndikubweretsera mzinda uwu ndi matauni ake onse masoka onse amene ndinanena, chifukwa anthu ake aumitsa mitima yawo nʼkukana* kumvera mawu anga.’”+
20 Tsopano Pasuri, mwana wa Imeri, wansembe, amenenso anali mtumiki wamkulu mʼnyumba ya Yehova, ankamvetsera pamene Yeremiya ankalosera zinthu zimenezi. 2 Kenako Pasuri anamenya mneneri Yeremiya n‘kumuika mʼmatangadza+ amene anali pa Geti Lakumtunda la Benjamini, limene linali mʼnyumba ya Yehova. 3 Ndiyeno pa tsiku lotsatira, Pasuri atamasula Yeremiya mʼmatangadzawo, Yeremiya anamuuza kuti:
“Yehova wanena kuti dzina lako silikhalanso Pasuri koma Chochititsa Mantha Paliponse.+ 4 Chifukwa Yehova wanena kuti, ‘Ine ndikukuchititsa kuti ukhale chinthu chochititsa mantha kwa iwe ndi kwa anzako onse, ndipo adzaphedwa ndi lupanga la adani awo iweyo ukuona.+ Anthu onse a mu Yuda ndidzawapereka mʼmanja mwa mfumu ya ku Babulo. Ena adzapita nawo ku Babulo ndipo ena adzawapha ndi lupanga.+ 5 Ndipo chuma chonse chamumzindawu, katundu wawo yense, zinthu zawo zonse zamtengo wapatali ndi chuma chonse cha mafumu a Yuda ndidzazipereka mʼmanja mwa adani awo.+ Adaniwo adzatenga zinthu zimenezi nʼkupita nazo ku Babulo.+ 6 Koma iwe Pasuri ndi anthu onse amene amakhala mʼnyumba yako, mudzapita ku ukapolo. Iweyo udzapita ku Babulo ndipo udzafera kumeneko nʼkuikidwa mʼmanda komweko limodzi ndi anzako onse, chifukwa walosera zabodza kwa iwo.’”+
7 Mwandipusitsa* inu Yehova, ndithu mwandipusitsa.
Mwagwiritsa ntchito mphamvu zanu pa ine ndipo mwapambana.+
Ndakhala chinthu choseketsa tsiku lonse.
Aliyense akungondinyoza.+
8 Nthawi zonse ndikafuna kulankhula, ndimafuula kuti,
“Chiwawa ndi chiwonongeko!”
Kwa ine mawu a Yehova achititsa kuti ndizinyozedwa ndi kusekedwa tsiku lonse.+
9 Choncho ndinanena kuti: “Sindidzanenanso za iye,
Ndipo sindidzalankhulanso mʼdzina lake.”+
Koma mumtima mwangamu, mawu ake anali ngati moto woyaka umene watsekeredwa mʼmafupa anga,
Ndipo ndinatopa ndi kudziletsa kuti ndisalankhule
Moti sindikanathanso kupirira.+
10 Chifukwa ndinamva mphekesera zambiri zoipa.
Zinthu zochititsa mantha zinali paliponse.+
Iwo ankanena kuti, “Muimbeni mlandu, tiyeni timuimbe mlandu!”
Munthu aliyense amene ankandifunira zabwino ankayembekezera kuti ndichite chinachake cholakwika.+
Ankanena kuti: “Mwina alakwitsa chinachake ameneyu,
Ndipo timugonjetsa nʼkumubwezera.”
11 Koma Yehova anali nane ngati msilikali woopsa.+
Nʼchifukwa chake anthu amene akundizunza adzakhumudwa ndipo sadzapambana.+
Adzachita manyazi kwambiri chifukwa zinthu sizidzawayendera bwino.
Manyazi awo adzakhala nawo mpaka kalekale ndipo sadzaiwalika.+
12 Koma inu Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, mumafufuza munthu wolungama.
13 Imbirani Yehova! Tamandani Yehova!
Chifukwa wapulumutsa munthu wosauka mʼmanja mwa anthu ochita zoipa.
14 Litembereredwe tsiku limene ndinabadwa!
Tsiku limene mayi anga anandibereka lisadalitsike!+
15 Atembereredwe munthu amene anabweretsa uthenga wabwino kwa bambo anga powauza kuti:
“Mkazi wako wakuberekera mwana wamwamuna, kamnyamata!”
Nʼkuchititsa kuti bambo anga asangalale kwambiri.
16 Munthu ameneyo akhale ngati mizinda imene Yehova anaigonjetsa popanda kuimvera chisoni.
Mʼmawa kwambiri azimva kulira kofuula ndipo masana azimva phokoso lochenjeza.
17 Nʼchifukwa chiyani sanandiphe ndili mʼmimba,
Kuti mayi anga akhale manda anga,
Ndiponso kuti apitirize kukhala oyembekezera?+
18 Nʼchifukwa chiyani ndinabadwa?
Kodi ndinabadwa kuti ndidzaone mavuto komanso kukhala wachisoni,
Kuti moyo wanga uthe mochititsa manyazi?+
21 Yeremiya analandira mawu ochokera kwa Yehova pamene Mfumu Zedekiya+ inatumiza Pasuri+ mwana wa Malikiya ndi Zefaniya+ mwana wa Maaseya, wansembe, kuti akamupemphe kuti: 2 “Chonde tifunsire kwa Yehova chifukwa Nebukadinezara,* mfumu ya ku Babulo, akufuna kuchita nafe nkhondo.+ Mwina Yehova atichitira imodzi mwa ntchito zake zodabwitsa moti Nebukadinezarayo atichokera.”+
3 Yeremiya anawauza kuti: “Mukauze Zedekiya kuti, 4 ‘Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti: “Ine ndichititsa zida zankhondo zimene zili mʼmanja mwanu kukutembenukirani. Zimenezi ndi zida zimene mukugwiritsa ntchito pomenyana ndi mfumu ya Babulo+ ndi Akasidi amene akuzungulirani kunja kwa mpanda wanu. Ndipo ine ndidzasonkhanitsa zidazo pakati pa mzindawu. 5 Ine ndidzamenyana nanu+ ndi mkono wotambasula ndiponso dzanja lamphamvu. Ndidzachita zimenezi nditakwiya, nditapsa mtima komanso ndili ndi ukali waukulu.+ 6 Ndidzapha onse okhala mumzindawu, anthu komanso nyama. Adzafa ndi mliri waukulu.”’*+
7 ‘Yehova wanena kuti: “Kenako Zedekiya mfumu ya Yuda, atumiki ake ndi anthu amumzindawu, onse amene adzapulumuke ku mliri, lupanga ndi njala yaikulu, ndidzawapereka mʼmanja mwa Mfumu Nebukadinezara* ya ku Babulo. Ndidzawapereka mʼmanja mwa adani awo komanso mʼmanja mwa amene akufuna kuchotsa moyo wawo.+ Nebukadinezara adzawapha ndi lupanga ndipo sadzawamvera chisoni, kuwakomera mtima kapena kuwachitira chifundo.”’+
8 Ndipo anthu awa uwauze kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Ine ndikuika njira ya moyo ndi njira ya imfa pamaso panu. 9 Anthu amene adzatsale mumzindawu adzafa ndi lupanga, njala ndiponso mliri. Koma aliyense amene adzatuluke nʼkupita kukadzipereka mʼmanja mwa Akasidi amene akuzungulirani, adzakhalabe ndi moyo. Iye adzapulumutsa moyo wake.”’+
10 ‘“Ndatsimikiza kubweretsa tsoka pamzinda uwu, osati zinthu zabwino,”*+ akutero Yehova. “Mzindawu udzaperekedwa mʼmanja mwa mfumu ya Babulo+ ndipo adzauwotcha ndi moto.”+
11 A mʼnyumba ya mfumu ya Yuda ukawauze kuti: Imvani zimene Yehova wanena. 12 Inu a mʼnyumba ya Davide, Yehova wanena kuti:
“Mʼmawa uliwonse muziweruza mwachilungamo
Ndipo muzipulumutsa munthu amene akuberedwa mʼmanja mwa anthu akuba mwachinyengo,+
Kuti mkwiyo wanga usayake ngati moto.+
Usayake popanda aliyense wouzimitsa
Chifukwa cha zinthu zoipa zimene mukuchita.”’+
13 ‘Iwe amene umakhala mʼchigwa, ine ndakuukira,
Iwe thanthwe limene lili pamalo afulati,’ akutero Yehova.
‘Koma inu amene mukunena kuti: “Kodi ndi ndani amene adzabwere kuno kuti atiukire?
Ndipo ndi ndani amene adzabwere mʼmalo athu okhala?”
14 Ndidzakupatsani chilango
Mogwirizana ndi zochita zanu,’+ akutero Yehova.
‘Ndipo ndidzayatsa moto munkhalango za mzindawu,
Moti udzapsereza zinthu zonse zimene zili pafupi ndi mzindawu.’”+
22 Yehova wanena kuti: “Pita kunyumba ya mfumu ya Yuda ndipo ukanene mawu awa. 2 Ukanene kuti, ‘Tamverani mawu a Yehova, inu mfumu ya Yuda amene mwakhala pampando wachifumu wa Davide. Mumve mawu amenewa inuyo, atumiki anu komanso anthu anu amene amalowa pamageti awa. 3 Yehova wanena kuti: “Muzichita zinthu motsatira malamulo komanso mwachilungamo. Muzipulumutsa munthu amene akuberedwa mʼmanja mwa munthu wakuba mwachinyengo. Musamachitire nkhanza mlendo aliyense amene akukhala mʼdziko lanu ndipo musamavulaze mwana wamasiye kapena mkazi wamasiye.+ Musamakhetse magazi a munthu aliyense wosalakwa mumzinda uno.+ 4 Mukamvera mawu amenewa mosamala, mafumu amene amakhala pampando wachifumu wa Davide+ adzalowa pamageti a nyumba iyi. Iwowo, atumiki awo komanso anthu awo adzalowa pamageti amenewa atakwera magaleta ndi mahatchi.”’+
5 ‘Koma mukapanda kumvera mawu amenewa, ndikulumbira pa dzina langa kuti nyumba iyi idzakhala bwinja,’ akutero Yehova.+
6 Ponena za nyumba ya mfumu ya Yuda, Yehova wanena kuti,
‘Kwa ine, iwe uli ngati Giliyadi,
Uli ngati nsonga ya phiri la ku Lebanoni.
Koma ndidzakusandutsa chipululu,
Ndipo mʼmizinda yako yonse simudzapezeka aliyense wokhalamo.+
7 Ndidzakutumizira anthu oti akuwononge,
Aliyense adzabwera ndi zida zake.+
Iwo adzadula mitengo yako ya mkungudza yabwino kwambiri
Ndipo adzaigwetsera pamoto.+
8 Anthu ochokera mʼmitundu yambiri adzadutsa pafupi ndi mzindawu ndipo adzafunsana kuti: “Nʼchifukwa chiyani Yehova anachitira mzinda waukuluwu zinthu zimenezi?”+ 9 Ndipo adzayankha kuti: “Chifukwa chakuti anthu amumzindawu anasiya pangano la Yehova Mulungu wawo nʼkuyamba kulambira milungu ina ndiponso kuitumikira.”’+
10 Munthu wakufa musamulire,
Ndipo musamumvere chisoni.
Mʼmalomwake, mulirire kwambiri munthu amene watengedwa kupita kudziko lina,
Chifukwa sadzabwereranso kudzaona dziko limene anabadwira.
11 Ponena za Salumu*+ mwana wa Yosiya, mfumu ya Yuda, amene akulamulira mʼmalo mwa bambo ake Yosiya,+ amene anachoka mʼdziko lino kupita ku ukapolo, Yehova wanena kuti: ‘Sadzabwereranso kwawo. 12 Chifukwa akafera kudziko laukapolo kumene amutengera ndipo dziko lino sadzalionanso.’+
13 Tsoka kwa munthu amene amamanga nyumba yake
Komanso zipinda zake zamʼmwamba mopanda chilungamo.
Amene amagwiritsa anthu ntchito kwaulere,
Ndipo amakana kuwapatsa malipiro awo.+
14 Amene amanena kuti, ‘Ndimanga nyumba yaikulu
Yokhala ndi zipinda zikuluzikulu zamʼmwamba.
Ndidzaiikira mawindo
Nʼkuyala matabwa a mkungudza mʼmakoma ake ndipo ndidzaipaka penti wofiira.’
15 Kodi ukuganiza kuti upitiriza kulamulira chifukwa chakuti ukugwiritsa ntchito kwambiri matabwa a mkungudzawa kuposa anthu ena?
Bambo akonso ankadya komanso kumwa
Koma ankachita zinthu motsatira malamulo komanso mwachilungamo,+
Ndipo zinthu zinawayendera bwino.
16 Ankateteza anthu ovutika komanso osauka pa mlandu,
Moti zinthu zinkayenda bwino.
‘Kodi kumeneku sindiye kundidziwa?’ akutero Yehova.
17 ‘Koma maso ako ndi mtima wako zili pa kupeza phindu mwachinyengo,
Kukhetsa magazi a anthu osalakwa,
Komanso kuba mwachinyengo ndi kulanda anthu zinthu zawo basi.’
18 Choncho ponena za Yehoyakimu+ mwana wa Yosiya, mfumu ya Yuda, Yehova wanena kuti,
‘Sadzamulira ngati mmene anthu amachitira kuti:
“Mayo ine mchimwene wanga! Mayo ine mchemwali wanga!”
Sadzamulira kuti:
“Mayo ine mbuye wanga! Mayo ine a mfumu aja!”
19 Adzaikidwa mʼmanda ngati mmene amaikira bulu,+
Adzamukoka kudutsa naye pamageti a Yerusalemu
Nʼkukamutaya kunja.’+
20 Pita ku Lebanoni ndipo ukalire,
Ukalire mofuula ku Basana
Ndipo ukalirenso ku Abarimu,+
Chifukwa onse amene ankakukonda kwambiri agonjetsedwa.+
21 Ndinalankhula nawe pamene unkaona kuti ndiwe wotetezeka.
Koma iwe unanena kuti, ‘Sindimvera.’+
Wakhala ukuchita zimenezi kuyambira uli wachinyamata,
Chifukwa wakhala usakumvera mawu anga.+
22 Mphepo idzaweta abusa ako onse+
Ndipo anthu amene akukukonda kwambiri adzatengedwa kupita ku ukapolo.
Pa nthawi imeneyo udzachititsidwa manyazi ndipo udzanyozeka chifukwa cha masoka onse amene adzakugwere.
23 Inu amene mumakhala mu Lebanoni,+
Amene mukukhala mʼnyumba zamitengo ya mkungudza,+
Mudzabuula kwambiri mukadzayamba kumva zowawa,
24 ‘Pali ine, Mulungu wamoyo,’ akutero Yehova, ‘ngakhale iwe Koniya*+ mwana wa Yehoyakimu,+ mfumu ya Yuda, utakhala mphete yodindira kudzanja langa lamanja, ndingakuvule! 25 Ndidzakupereka mʼmanja mwa anthu amene akufuna kuchotsa moyo wako, mʼmanja mwa anthu amene umawaopa, mʼmanja mwa Mfumu Nebukadinezara* ya ku Babulo ndiponso mʼmanja mwa Akasidi.+ 26 Iwe ndi mayi ako amene anakubereka, ndidzakuponyerani kudziko lina limene simunabadwireko ndipo mudzafera kumeneko. 27 Ndipo iwo sadzabwereranso kudziko limene akulilakalaka.+
28 Kodi munthu uyu Koniya, wangokhala chiwiya chonyozeka komanso chophwanyika,
Chiwiya chimene palibe amene akuchifuna?
Nʼchifukwa chiyani iyeyu ndi ana ake agwetsedwa pansi
Nʼkuponyedwa mʼdziko limene sakulidziwa?’+
29 Iwe dziko lapansi, dziko lapansi, dziko lapansi, tamvera mawu a Yehova.
30 Yehova wanena kuti:
‘Lembani kuti munthu uyu alibe ana,
Munthu amene zinthu sizidzamuyendera bwino pa moyo wake.*
Chifukwa palibe mwana wake aliyense, amene adzakwanitse
Kukhala pampando wachifumu wa Davide nʼkuyambiranso kulamulira mu Yuda.’”+
23 “Tsoka abusa amene akuwononga ndi kubalalitsa nkhosa zapamalo anga odyetsera ziweto!” akutero Yehova.+
2 Choncho Yehova Mulungu wa Isiraeli wadzudzula abusa amene akuweta anthu ake kuti: “Inu mwabalalitsa nkhosa zanga. Munapitiriza kuzimwaza ndipo simunazisamalire.”+
“Tsopano ndikulangani chifukwa cha zochita zanu zoipa,” akutero Yehova.
3 “Kenako ndidzasonkhanitsa pamodzi nkhosa zanga zotsala kuchokera mʼmayiko onse kumene ndinazibalalitsira+ ndipo ndidzazibwezeretsa kumalo awo kumene zimadyera.+ Nkhosazo zidzaberekana ndi kuchuluka.+ 4 Ndidzapatsa nkhosazo abusa amene adzaziwete moyenerera.+ Sizidzaopanso kanthu kapena kuchita mantha ndipo palibe imene idzasowe,” akutero Yehova.
5 “Taonani! Masiku adzafika,” watero Yehova, “pamene ndidzaike mfumu yolungama pampando wachifumu yochokera mʼbanja lachifumu la Davide.*+ Mfumuyo idzalamulira mʼdzikoli+ ndipo idzachita zinthu mwanzeru, motsatira malamulo komanso mwachilungamo.+ 6 Mʼmasiku a mfumu imeneyi, Yuda adzapulumutsidwa+ ndipo Isiraeli adzakhala motetezeka.+ Dzina la mfumuyi lidzakhala: Yehova Ndi Chilungamo Chathu.”+
7 “Koma masiku akubwera,” akutero Yehova, “pamene sadzalumbiranso kuti, ‘Pali Yehova Mulungu wamoyo amene anatulutsa Aisiraeli mʼdziko la Iguputo.’+ 8 Koma adzalumbira kuti, ‘Pali Yehova Mulungu wamoyo amene anatulutsa a mʼnyumba ya Isiraeli nʼkuwabweretsa kuno kuchokera mʼdziko lakumpoto komanso kuchokera mʼmayiko onse kumene ndinawabalalitsiraʼ ndipo adzakhala mʼdziko lawo.”+
9 Ponena za aneneriwo ndikuti:
Mtima wanga wasweka mkati mwanga.
Mafupa anga onse akunjenjemera.
Ndili ngati munthu woledzera
Komanso ngati munthu amene wagonjetsedwa ndi vinyo,
Chifukwa cha Yehova komanso chifukwa cha mawu ake oyera.
10 Dzikoli ladzaza ndi anthu achigololo.+
Chifukwa cha matemberero, dziko likulira maliro+
Ndipo malo amʼchipululu odyetserako ziweto auma.+
Zochita za anthuwa ndi zoipa ndipo akugwiritsa ntchito mphamvu zawo molakwika.
11 “Aneneri ndi ansembe, onse aipitsidwa.*+
Ndipo ngakhale mʼnyumba mwanga ndapezamo zoipa zimene akuchita,”+ akutero Yehova.
12 “Choncho njira zawo zidzakhala zoterera komanso zamdima.+
Adzakankhidwa ndipo adzagwa.
Chifukwa ndidzawagwetsera tsoka
Mʼchaka chimene ndidzawalange,” akutero Yehova.
13 “Ndaona zinthu zonyansa mwa aneneri a ku Samariya.+
Iwo akulosera mʼdzina la Baala
Ndipo akusocheretsa anthu anga, Aisiraeli.
14 Mwa aneneri a ku Yerusalemu ndaona zinthu zoopsa.
Iwo akuchita chigololo+ ndiponso akuchita zinthu mwachinyengo.+
Akulimbikitsa* anthu ochita zoipa
Ndipo sakusiya zinthu zoipa zimene akuchita.
15 Choncho Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wadzudzula aneneriwo kuti:
“Ndiwadyetsa chitsamba chowawa
Ndipo ndiwapatsa madzi apoizoni kuti amwe.+
Chifukwa kuchokera mwa aneneri a ku Yerusalemu mpatuko wafalikira mʼdziko lonse.”
16 Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti:
“Musamvere mawu a aneneri amene akulosera kwa inu.+
Iwo akungokupusitsani.*
17 Mobwerezabwereza iwo akuuza anthu amene sakundilemekeza kuti,
‘Yehova wanena kuti: “Inu mudzakhala pa mtendere.”’+
Ndipo aliyense amene amatsatira mtima wake woipawo akumuuza kuti,
‘Tsoka silidzakugwerani.’+
18 Ndi ndani amene waimirira pagulu la anthu amene Yehova amawakonda
Kuti azindikire ndi kumva mawu ake?
Ndi ndani amene watchera khutu kuti amvetsere mawu ake?
19 Taonani! Mkwiyo wa Yehova udzawomba ngati mphepo yamkuntho.
Udzawomba ngati kamvulumvulu wamphamvu pamitu ya anthu oipa.+
20 Mkwiyo wa Yehova sudzabwerera
Mpaka atachita ndi kukwaniritsa zofuna za mtima wake.
Zinthu zimenezi mudzazimvetsa bwino mʼmasiku otsiriza.
21 “Ine sindinatumize aneneriwo, koma anathamanga.
Ine sindinalankhule nawo, koma analosera.+
22 Koma ngati akanaima pagulu la anthu amene ndimawakonda,
Akanachititsa kuti anthu anga amve mawu anga
Ndipo akanawachititsa kuti abwerere nʼkusiya kuyenda mʼnjira zawo zoipa komanso kusiya zochita zawo zoipa.”+
23 Yehova wanena kuti: “Kodi ine ndimakhala Mulungu pamene ndili pafupi basi, osati pamenenso ndili patali?”
24 “Kodi pali munthu amene angabisale pamalo obisika amene ine sindingamuone?”+ akutero Yehova.
“Kodi kumwamba kapena padziko lapansi, pali chilichonse chimene sindingachione?”+ akutero Yehova.
25 “Ndamva aneneri amene akulosera zinthu zabodza mʼdzina langa akunena kuti, ‘Ndalota maloto! Ndalota maloto!’+ 26 Kodi maganizo onena zabodza apitiriza kukhala mumtima mwa aneneriwa mpaka liti? Iwo ndi aneneri amene amanena chinyengo chochokera mumtima mwawo.+ 27 Iwo akufuna kuchititsa kuti anthu anga aiwale dzina langa pogwiritsa ntchito maloto amene aneneriwo amauzana, mofanana ndi mmene makolo awo anaiwalira dzina langa chifukwa cha Baala.+ 28 Mneneri amene walota maloto anene maloto akewo. Koma amene ndamuuza mawu anga, azinena zoona polankhula mawu angawo.”
“Kodi mapesi a tirigu angafanane ndi tirigu weniweniyo?” akutero Yehova.
29 Yehova wanena kuti: “Kodi mawu anga safanana ndi moto?+ Kodi safanana ndi hamala imene imaphwanya thanthwe?”+
30 “Choncho ine ndidzalanga aneneriwo chifukwa aliyense wa iwo akuba mawu anga kwa mnzake,” akutero Yehova.+
31 Yehova wanena kuti: “Ine ndidzalanga aneneri amene akugwiritsa ntchito lilime lawo nʼkumanena kuti, ‘Awa ndi mawu ochokera kwa Mulungu!’”+
32 “Ine ndidzalanga aneneri amene akulota maloto abodza, amene akunena malotowo nʼkusocheretsa anthu anga chifukwa cha mabodza awo komanso kudzitama kwawo,” akutero Yehova.+
“Koma ine sindinawatume kapena kuwalamula kuti achite zimenezo. Choncho zochita zawo sizidzapindulitsa anthu awa ngakhale pangʼono,”+ akutero Yehova.
33 “Ndipo anthu awa komanso mneneri kapena wansembe akakufunsa kuti, ‘Kodi uthenga* wa Yehova ukuti chiyani?’ uwayankhe kuti, ‘“Anthu inu ndinu katundu wolemera! Ndipo ndidzakutayani,”+ akutero Yehova.’ 34 Mneneri, wansembe kapena aliyense amene akunena kuti, ‘Uthenga uwu ndi katundu wolemera wa Yehova!’ ndidzalanga munthuyo ndi anthu a mʼnyumba yake. 35 Aliyense wa inu akufunsa mnzake ndi mʼbale wake kuti, ‘Kodi Yehova wayankha kuti chiyani? Ndipo Yehova wanena kuti chiyani?’ 36 Koma musanenenso kuti uthenga wa Yehova ndi katundu wolemera, chifukwa katundu wolemera ndi mawu a aliyense wa inu ndipo mwasintha mawu a Mulungu wathu wamoyo, Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.
37 Mneneri umufunse kuti, ‘Kodi Yehova wakuyankha chiyani? Ndipo Yehova wanena kuti chiyani? 38 Mukapitiriza kunena kuti, “Uthenga uwu ndi katundu wolemera wa Yehova!” Yehova wanena kuti: “Chifukwa chakuti mukunenabe kuti, ‘Mawu a Yehova ndi katundu wolemera,’ ngakhale kuti ndinakuuzani kuti ‘Musamanene kuti: “Mawu a Yehova ndi katundu wolemera!”’ 39 tamverani, ine ndikunyamulani nʼkukutayani kutali ndi ine. Ndidzachita zimenezi kwa inuyo ndi mzinda umene ndinapatsa inu ndi makolo anu. 40 Ndidzachititsa kuti mukhale ndi manyazi mpaka kalekale ndipo mudzanyozeka mpaka kalekale. Zimenezi sizidzaiwalika.”’”+
24 Kenako Yehova anandionetsa madengu awiri a nkhuyu amene anali patsogolo pa kachisi wa Yehova. Anandionetsa madenguwo pambuyo poti Nebukadinezara* mfumu ya Babulo watenga Yekoniya*+ mwana wa Yehoyakimu,+ mfumu ya Yuda, pamodzi ndi akalonga a Yuda, amisiri komanso anthu osula zitsulo,* kuchoka ku Yerusalemu nʼkupita nawo ku ukapolo ku Babulo.+ 2 Dengu limodzi linali ndi nkhuyu zabwino kwambiri ngati nkhuyu zoyambirira kucha. Koma dengu lina linali ndi nkhuyu zoipa kwambiri. Zinali zoipa kwambiri moti munthu sakanatha kuzidya.
3 Kenako Yehova anandifunsa kuti: “Kodi ukuona chiyani Yeremiya?” Ndipo ine ndinayankha kuti: “Ndikuona nkhuyu. Nkhuyu zabwino, nʼzabwino kwambiri koma nkhuyu zoipa, nʼzoipa kwambiri. Ndi zoipa kwambiri moti munthu sangadye.”+
4 Ndiyeno Yehova anandiuza kuti: 5 “Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Anthu amene anatengedwa ku Yuda kupita ku ukapolo, amene ndinawachotsa mʼdziko lino nʼkuwatumiza kudziko la Akasidi ali ngati nkhuyu zabwino zimenezi. Ndidzawaona kuti ndi anthu abwino. 6 Maso anga adzakhala pa iwo kuti ndiwachitire zabwino ndipo ndidzachititsa kuti abwerere mʼdziko lino.+ Ndidzachititsa kuti zinthu ziziwayendera bwino ndipo sindidzawawononga. Ndidzawadzala ndipo sindidzawazula.+ 7 Ndidzawapatsa mtima woti andidziwe kuti ine ndine Yehova.+ Iwo adzakhala anthu anga ndipo ine ndidzakhala Mulungu wawo+ chifukwa adzabwerera kwa ine ndi mtima wawo wonse.+
8 Koma mofanana ndi nkhuyu zoipa zija, zimene ndi zoipa kwambiri moti munthu sangathe kudya,+ Yehova wanena kuti: “Ndi mmenenso ndidzaonere Zedekiya+ mfumu ya Yuda, akalonga ake, anthu onse opulumuka mu Yerusalemu amene atsalira mʼdzikoli komanso anthu okhala mʼdziko la Iguputo.+ 9 Ndidzachititsa kuti anthu a mitundu yonse padziko lapansi achite mantha akadzaona tsoka limene ndidzawabweretsere.+ Anthu adzawanyoza, adzawaona kuti ndi chitsanzo cha anthu amene akumana ndi tsoka, adzawaseka komanso kuwatemberera+ kulikonse kumene ndidzawabalalitsire.+ 10 Ndidzawatumizira lupanga,+ njala ndi mliri,*+ mpaka adzatheratu mʼdziko limene ndinapereka kwa iwowo ndi makolo awo.”’”
25 Awa ndi mawu amene Yeremiya anauzidwa onena za anthu onse a mu Yuda mʼchaka cha 4 cha ulamuliro wa Yehoyakimu+ mwana wa Yosiya, mfumu ya Yuda, chimenenso chinali chaka choyamba cha ulamuliro wa Nebukadinezara* mfumu ya Babulo. 2 Mneneri Yeremiya analankhula mawu amenewa ponena za anthu onse a mu Yuda komanso anthu onse amene ankakhala mu Yerusalemu kuti:
3 “Kuyambira mʼchaka cha 13 cha ulamuliro wa Yosiya+ mwana wa Amoni, mfumu ya Yuda, mpaka lero, zaka 23 zonsezi, Yehova wakhala akundiuza mawu ndipo ine ndakhala ndikukuuzani mawuwo mobwerezabwereza,* koma inu simunamvere.+ 4 Yehova anakutumizirani atumiki ake onse omwe anali aneneri. Ankawatumiza mobwerezabwereza* koma inu simunawamvere kapena kutchera khutu lanu kuti mumvetsere.+ 5 Iwo ankakuuzani kuti, ‘Chonde, aliyense wa inu atembenuke nʼkusiya njira zake zoipa ndi zochita zake zoipa.+ Mukatero mudzapitiriza kukhala kwa nthawi yaitali mʼdziko limene Yehova anakupatsani kalekale, inuyo ndi makolo anu. 6 Musatsatire milungu ina nʼkumaitumikira komanso kuigwadira nʼkundikhumudwitsa ndi ntchito ya manja anu. Mukachita zimenezi ndidzakugwetserani tsoka.’
7 ‘Koma simunandimvere,’ akutero Yehova, ‘Mʼmalomwake munandikhumudwitsa ndi ntchito ya manja anu, zimene zinachititsa kuti tsoka likugwereni.’+
8 Choncho Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti, ‘“Chifukwa simunamvere mawu anga, 9 ndikuitana mafuko onse akumpoto,”+ akutero Yehova, “ndikuitananso Mfumu Nebukadinezara* ya ku Babulo, mtumiki wanga.+ Ndibweretsa anthu amenewa kuti aukire dziko lino+ ndi anthu amene akukhala mmenemo komanso mitundu yonse imene yakuzungulirani.+ Ndidzakuwonongani inuyo ndi mitundu yonse yokuzungulirani ndipo ndidzakusandutsani chinthu chochititsa mantha chimene anthu azidzachiimbira mluzu ndipo malo anu adzakhala mabwinja mpaka kalekale. 10 Ndidzathetsa phokoso lachikondwerero ndi phokoso lakusangalala mʼmalowo.+ Ndidzathetsanso mawu osangalala a mkwati ndi a mkwatibwi.+ Simudzamvekanso kupera kwa mphero ndipo simudzaonekanso kuwala kwa nyale. 11 Dziko lonseli lidzakhala bwinja ndipo lidzakhala chinthu chochititsa mantha. Mitundu imeneyi idzatumikira mfumu ya ku Babulo zaka 70.”’+
12 ‘Ndiyeno zaka 70 zimenezo zikadzakwana,+ ndidzalanga mfumu ya Babulo ndi mtundu umenewo chifukwa cha zolakwa zawo.+ Ndipo dziko la Akasidi ndidzalisandutsa bwinja mpaka kalekale,’ akutero Yehova.+ 13 Mawu anga onse amene ndanena okhudza zimene ndidzachitire dzikolo ndidzawakwaniritsa. Ndidzakwaniritsa zonse zimene zalembedwa mʼbuku ili, zimene Yeremiya wanenera kuti zidzachitikira mitundu yonse. 14 Chifukwa mitundu yambiri ndi mafumu otchuka+ adzawagwiritsa ntchito ngati akapolo+ ndipo ndidzawabwezera mogwirizana ndi zochita zawo komanso ntchito ya manja awo.’”+
15 Yehova Mulungu wa Isiraeli anandiuza kuti: “Tenga kapu iyi ya vinyo wa mkwiyo imene ili mʼdzanja langa ndipo ukamwetse mitundu yonse imene ndikukutumizako. 16 Iwo akamwa nʼkuyamba kudzandira komanso kuchita zinthu ngati amisala chifukwa cha lupanga limene ndikuwatumizira pakati pawo.”+
17 Choncho ndinatenga kapu imene inali mʼdzanja la Yehova ndipo ndinamwetsa mitundu yonse imene Yehova ananditumizako. Mitunduyo ndi iyi:+ 18 kuyamba ndi Yerusalemu ndi mizinda ya Yuda+ komanso mafumu ake ndi akalonga ake. Ndinawamwetsa kuti mizinda yawo ikhale bwinja, chinthu chochititsa mantha chimene anthu azidzachiimbira mluzu ndiponso kuti ikhale yotembereredwa+ ngati mmene zilili lero. 19 Kenako ndinamwetsanso Farao mfumu ya Iguputo, atumiki ake, akalonga ake ndi anthu ake onse+ 20 ndiponso anthu a mitundu yosiyanasiyana. Mafumu onse amʼdziko la Uzi, mafumu onse amʼdziko la Afilisiti,+ Asikeloni,+ Gaza, Ekironi komanso amene anatsala ku Asidodi, 21 Edomu,+ Mowabu+ ndi Aamoni,+ 22 mafumu onse a Turo, mafumu onse a Sidoni+ ndi mafumu a pachilumba chamʼnyanja. 23 Ndinamwetsanso Dedani,+ Tema, Buza, onse odulira ndevu zawo zamʼmbali,+ 24 mafumu onse a Aluya,+ mafumu onse a anthu a mitundu yosiyanasiyana amene amakhala mʼchipululu, 25 mafumu onse a Zimiri, mafumu onse a Elamu,+ mafumu onse a Amedi,+ 26 mafumu onse akumpoto, akutali ndi apafupi, mmodzi ndi mmodzi ndipo ndinamwetsanso maufumu ena onse apadziko lapansi. Koma mfumu ya Sesaki*+ idzamwa pambuyo pa onsewa.
27 “Ndiyeno ukawauze kuti, ‘Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Mulungu wa Isiraeli wanena kuti: “Imwani ndipo muledzere, musanze ndi kugwa osadzukanso+ chifukwa cha lupanga limene ndikutumiza pakati panu.”’ 28 Ngati angakakane kulandira kapuyi mʼmanja mwako kuti amwe, ukawauze kuti, ‘Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti: “Mukuyenera kumwa basi. 29 Tamverani! Ngati ndikuyamba kubweretsa tsoka pa mzinda umene ukutchedwa ndi dzina langa,+ ndiye kodi inuyo simukuyenera kulandira chilango?”’+
‘Simulephera kulangidwa chifukwa ndikuitana lupanga kuti liwononge anthu onse amene akukhala padziko lapansi,’ akutero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.
30 Ndiyeno iweyo unenere mawu onsewa ndipo anthuwo uwauze kuti,
‘Yehova adzabangula ali kumwamba,
Ndipo adzachititsa kuti mawu ake amveke ali kumalo ake oyera kumene amakhala.
Iye adzabangula kwambiri polengeza chiweruzo chake kwa anthu amene akukhala mʼmalo ake.
Adzafuula mosangalala ngati anthu amene akuponda mphesa,
Adzaimba posonyeza kuti wapambana polimbana ndi anthu onse amene akukhala padziko lapansi.’
31 ‘Phokoso lidzamveka kumalekezero a dziko lapansi,
Chifukwa Yehova akufuna kuimba mlandu mitundu ya anthu.
Iye adzapereka yekha chiweruzo kwa anthu onse.+
Ndipo anthu oipa adzawapha ndi lupanga,’ akutero Yehova.
32 Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti:
‘Taonani! Tsoka likufalikira kuchokera ku mtundu wina kupita ku mtundu wina,+
Ndipo mkuntho wamphamvu udzafika kuchokera kumadera akutali kwambiri a dziko lapansi.+
33 Pa tsiku limenelo anthu amene adzaphedwe ndi Yehova adzachokera kumalekezero a dziko lapansi kukafika kumalekezero ena a dziko lapansi. Maliro awo sadzaliridwa, sadzawasonkhanitsa pamodzi kapena kuwaika mʼmanda. Iwo adzakhala ngati manyowa panthaka.’
34 Fuulani ndipo lirani abusa inu!
Gubuduzikani inu anthu olemekezeka pa gulu la nkhosa,
Chifukwa nthawi yoti muphedwe komanso yoti mubalalitsidwe yafika,
Ndipo mudzagwa ndi kuphwanyika ngati chiwiya chamtengo wapatali.
35 Abusa alibe malo othawirako,
Ndipo palibe njira imene anthu olemekezeka pa gulu la nkhosa angadzere pothawa.
36 Tamverani! Abusa akufuula
Komanso anthu olemekezeka pa gulu la nkhosa akulira.
Chifukwa Yehova akuwononga malo awo odyetserako ziweto.
37 Malo okhala amtendere akhala opanda chamoyo chilichonse
Chifukwa cha mkwiyo woyaka moto wa Yehova.
38 Iye watuluka mʼmalo ake okhalamo ngati mkango wamphamvu,*+
Dziko lawo lakhala chinthu chochititsa mantha.
Chifukwa cha lupanga lake lankhanza
Komanso chifukwa cha mkwiyo wake woyaka moto.”
26 Kumayambiriro kwa ulamuliro wa Yehoyakimu+ mwana wa Yosiya, mfumu ya Yuda, Yehova anauza Yeremiya mawu akuti: 2 “Yehova wanena kuti, ‘Ukaimirire mʼbwalo la nyumba ya Yehova ndipo ukanene zimene zidzachitikire anthu onse amʼmizinda ya Yuda amene akubwera kudzalambira* panyumba ya Yehova. Ukawauze zonse zimene ndakulamula ndipo usachotsepo mawu ngakhale amodzi. 3 Mwina adzamvera ndipo aliyense wa iwo adzabwerera kuchoka panjira yake yoipa. Ndipo ndidzasintha maganizo anga okhudza tsoka limene ndikufuna kuwagwetsera chifukwa cha zochita zawo zoipa.+ 4 Ukawauze kuti: “Yehova wanena kuti, ‘Ngati simundimvera potsatira chilamulo changa chimene* ndakupatsani, 5 komanso kumvera mawu a atumiki anga omwe ndi aneneri, amene ndikuwatumiza kwa inu mobwerezabwereza,* omwe inu simunawamvere,+ 6 ine ndidzachititsa kuti nyumba iyi ikhale ngati Silo.+ Ndidzawononga mzindawu ndipo mitundu yonse yapadziko lapansi idzaugwiritsa ntchito ngati chitsanzo potemberera.’”’”+
7 Choncho ansembe, aneneri ndi anthu onse anamva Yeremiya akulankhula mawu amenewa mʼnyumba ya Yehova.+ 8 Ndiyeno Yeremiya atamaliza kulankhula mawu onse amene Yehova anamulamula kuti akauze anthu onse, nthawi yomweyo ansembe, aneneri ndi anthu onse anamugwira nʼkunena kuti: “Ukuyenera kufa basi. 9 Nʼchifukwa chiyani wanenera mʼdzina la Yehova kuti, ‘Nyumba iyi idzakhala ngati Silo ndipo mzinda uwu udzawonongedwa moti simudzapezeka aliyense wokhalamoʼ?” Ndiyeno anthu onse anabwera mʼnyumba ya Yehova nʼkuzungulira Yeremiya.
10 Akalonga a Yuda atamva mawu amenewa, anachoka kunyumba ya mfumu nʼkupita kunyumba ya Yehova ndipo anakakhala pakhomo lapageti latsopano la nyumba ya Yehova.+ 11 Ansembe ndi aneneri anauza akalongawo ndi anthu onse kuti: “Munthuyu akuyenera kuphedwa+ chifukwa wanenera zoti mzindawu udzakumana ndi tsoka monga mmene mwamvera ndi makutu anu.”+
12 Kenako Yeremiya anauza akalonga onse ndi anthu onsewo kuti: “Yehova ndi amene anandituma kuti ndidzanene mawu onse amene mwamva okhudza nyumbayi ndi mzindawu.+ 13 Choncho panopa sinthani njira zanu komanso zochita zanu ndipo muzimvera mawu a Yehova Mulungu wanu. Mukatero, Yehova adzasintha maganizo ake okhudza tsoka limene wanena kuti akugwetserani.+ 14 Koma ineyo, ndili mʼmanja mwanu. Ndichiteni zilizonse zimene mukuona kuti nʼzabwino ndi zoyenera. 15 Koma mudziwe kuti mukandipha, inuyo, mzindawu ndi anthu onse amene akukhala mumzindawu mukhala ndi mlandu wa magazi chifukwa chopha munthu wosalakwa. Ndithudi, Yehova ndi amene wandituma kuti ndidzakuuzeni mawu onse amene mwamvawa.”
16 Kenako akalonga ndi anthu onse anauza ansembe ndi aneneri kuti: “Munthu uyu sakuyenera kuphedwa chifukwa walankhula nafe mʼdzina la Yehova Mulungu wathu.”
17 Kuwonjezera pamenepo, akuluakulu ena amʼdzikolo anaimirira nʼkuyamba kuuza anthu onse amene anasonkhana kuti: 18 “Mika+ wa ku Moreseti nayenso ankanenera mʼmasiku a Mfumu Hezekiya+ ya ku Yuda. Iye ankauza anthu onse a ku Yuda kuti, ‘Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti:
“Ziyoni adzalimidwa ngati munda,
Yerusalemu adzakhala mabwinja,+
Ndipo phiri la nyumba ya Mulungu* lidzakhala ngati zitunda zamunkhalango.”’+
19 Kodi Hezekiya mfumu ya Yuda ndi anthu onse a mu Yuda anamupha? Kodi iye sanaope Yehova komanso kupempha Yehova kuti amukomere mtima?* Atatero, kodi Yehova sanasinthe maganizo ake pa tsoka limene ananena kuti adzawabweretsera?+ Pamenepatu ife tikudziitanira tsoka lalikulu.
20 Panalinso munthu wina amene ankanenera mʼdzina la Yehova. Iyeyu anali Uliya mwana wa Semaya wa ku Kiriyati-yearimu.+ Iye ananeneratu zimene zidzachitikire mzindawu mofanana ndi mawu a Yeremiya. 21 Ndiyeno Mfumu Yehoyakimu,+ asilikali ake onse amphamvu ndi akalonga onse anamva mawu amene Uliya ananena. Zitatero mfumu inakonza zoti imuphe.+ Uliya atamva zimenezo, nthawi yomweyo anachita mantha ndipo anathawira ku Iguputo. 22 Kenako Mfumu Yehoyakimu inatumiza Elinatani,+ mwana wa Akibori ndi amuna ena ku Iguputo. 23 Iwo anagwira Uliya nʼkubwera naye kwa Mfumu Yehoyakimu. Ndiyeno mfumuyo inapha Uliya ndi lupanga+ nʼkutaya mtembo wake mʼmanda a anthu wamba.”
24 Koma Ahikamu,+ mwana wa Safani+ anateteza Yeremiya, nʼchifukwa chake sanaperekedwe kwa anthu kuti amuphe.+
27 Kumayambiriro kwa ulamuliro wa Yehoyakimu mwana wa Yosiya, mfumu ya Yuda, Yehova anauza Yeremiya kuti akanene mawu akuti: 2 “Yehova wandiuza kuti, ‘Upange zomangira komanso magoli ndipo uzivale mʼkhosi mwako. 3 Kenako uzitumize kwa mfumu ya Edomu,+ mfumu ya Mowabu,+ mfumu ya Aamoni,+ mfumu ya Turo+ ndi mfumu ya Sidoni.+ Upatsire amithenga amene abwera ku Yerusalemu kudzaonana ndi Zedekiya mfumu ya Yuda. 4 Ukatero, uwalamule kuti akauze ambuye awo kuti:
“Mukauze ambuye anu kuti Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti, 5 ‘Ine ndi amene ndinapanga dziko lapansi, anthu ndi nyama zapadziko lapansi pogwiritsa ntchito mphamvu zanga zazikulu ndiponso dzanja langa lotambasula. Ndipo dziko lapansili ndalipereka kwa amene ndikufuna.*+ 6 Tsopano ndapereka mayiko onsewa mʼmanja mwa mtumiki wanga, Mfumu Nebukadinezara+ ya ku Babulo. Ndamupatsanso ngakhale nyama zakutchire kuti zimutumikire. 7 Mitundu yonse ya anthu idzatumikira iyeyo, mwana wake wamwamuna ndi mdzukulu wake mpaka idzafike nthawi yoti ufumu wake uthe.+ Pa nthawi imeneyo, mitundu yambiri ya anthu ndi mafumu amphamvu adzamupangitsa kuti akhale kapolo wawo.’+
8 ‘Ngati mtundu uliwonse wa anthu kapena ufumu udzakane kutumikira Mfumu Nebukadinezara ya ku Babulo komanso kukana kuika khosi lake mʼgoli la mfumu ya Babulo, ine ndidzalanga mtundu umenewo ndi lupanga,+ njala komanso mliri* mpaka nditauwononga wonse pogwiritsa ntchito dzanja la Nebukadinezara,’ akutero Yehova.
9 ‘Choncho musamvere aneneri, anthu ochita zamaula, olota maloto, ochita zamatsenga ndi obwebweta amene ali pakati panu ndipo akukuuzani kuti: “Simudzatumikira mfumu ya Babulo.” 10 Chifukwa anthu amenewa akulosera zabodza kwa inu, mukawamvera mudzatengedwa mʼdziko lanu nʼkupita dziko lakutali ndipo ine ndidzakubalalitsani moti mudzawonongedwa.
11 Koma mtundu wa anthu umene udzaike khosi lake mʼgoli la mfumu ya Babulo nʼkuitumikira, ndidzaulola kuti ukhalebe* mʼdziko lawo ndipo udzalima minda nʼkumakhala mʼdzikolo,’ akutero Yehova.”’”
12 Mfumu Zedekiya+ ya ku Yuda ndinaiuzanso mawu amenewa kuti: “Ikani makosi anu mʼgoli la mfumu ya Babulo nʼkuitumikira. Mutumikire mfumuyo ndi anthu ake kuti mukhalebe ndi moyo.+ 13 Kodi iweyo ndi anthu ako muferenji ndi lupanga,+ njala+ ndi mliri+ ngati mmene Yehova wanenera kuti ndi zimene zidzachitikire mtundu umene sudzatumikira mfumu ya Babulo? 14 Musamvere mawu a aneneri amene akukuuzani kuti, ‘Simudzatumikira mfumu ya Babulo,’+ chifukwa zimene akulosera kwa inuzo ndi zabodza.+
15 ‘Ine sindinawatume,’ akutero Yehova, ‘koma iwo akulosera zabodza mʼdzina langa. Mukawamvera ndidzakubalalitsani ndipo ndidzawononga inuyo limodzi ndi aneneri amene akulosera kwa inu.’”+
16 Ndiyeno ndinauza ansembe ndi anthu onsewo kuti: “Yehova wanena kuti, ‘Musamvere mawu a aneneri anu amene akulosera kwa inu kuti: “Taonani! Ziwiya zamʼnyumba ya Yehova zibwezedwa posachedwapa kuchokera ku Babulo!”+ chifukwa iwo akulosera zabodza kwa inu.+ 17 Musawamvere. Tumikirani mfumu ya Babulo kuti mupitirize kukhala ndi moyo.+ Kodi mzindawu ukhale bwinja chifukwa chiyani? 18 Koma ngati iwo ndi aneneri ndipo akulankhula mawu a Yehova, iwo apemphe kwa Yehova wa magulu ankhondo akumwamba kuti ziwiya zimene zinatsala mʼnyumba ya Yehova, mʼnyumba ya mfumu ya Yuda ndi zimene zinatsala ku Yerusalemu zisatengedwe kupita ku Babulo.’
19 Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena zokhudza zipilala,+ thanki ya madzi,*+ zotengera zamawilo+ ndi ziwiya zimene zatsala mumzindawu, 20 zimene Nebukadinezara mfumu ya Babulo sanatenge pamene ankatenga Yekoniya mwana wa Yehoyakimu, mfumu ya Yuda, pamodzi ndi olemekezeka onse a Yuda ndi Yerusalemu, kupita nawo ku ukapolo ku Babulo kuchokera ku Yerusalemu.+ 21 Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Mulungu wa Isiraeli, wanena zokhudza ziwiya zimene zinatsala mʼnyumba ya Yehova, mʼnyumba ya mfumu ya Yuda ndi zimene zinatsala ku Yerusalemu kuti: 22 ‘“Ziwiya zimenezi zidzapita ku Babulo+ ndipo zidzakhala kumeneko mpaka tsiku limene ndidzazikumbukire,” akutero Yehova. “Ndipo ndidzazitenga nʼkuzibwezeretsa pamalo ano.”’”+
28 Ndiyeno mʼchaka chomwecho, chaka cha 4, mʼmwezi wa 5, kumayambiriro kwa ulamuliro wa Zedekiya+ mfumu ya Yuda, mneneri Hananiya mwana wa Azuri, wa ku Gibiyoni,+ anauza Yeremiya mʼnyumba ya Yehova pamaso pa ansembe ndi anthu onse kuti: 2 “Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti, ‘Ndithyola goli la mfumu ya Babulo.+ 3 Zaka ziwiri zisanathe, ndibwezeretsa pamalo ano ziwiya zonse zamʼnyumba ya Yehova zimene Nebukadinezara mfumu ya Babulo anatenga kuno nʼkupita nazo ku Babulo.’”+ 4 “‘Ndipo Yekoniya+ mwana wa Yehoyakimu,+ mfumu ya Yuda, ndiponso anthu onse a mu Yuda amene anatengedwa kupita ku ukapolo ku Babulo+ ndiwabwezeretsa kuno, chifukwa ndidzathyola goli la mfumu ya Babulo,’ akutero Yehova.”
5 Kenako mneneri Yeremiya anayankha mneneri Hananiya pamaso pa ansembe ndi anthu onse amene anaimirira mʼnyumba ya Yehova. 6 Mneneri Yeremiya anayankha kuti: “Zikhale momwemo!* Yehova achitedi zimenezo! Yehova akwaniritse mawu ako amene walosera. Achite zimenezo pobwezeretsa pamalo ano ziwiya zamʼnyumba ya Yehova ndi anthu onse amene anatengedwa kupita ku ukapolo ku Babulo! 7 Komabe, tamvera uthenga uwu umene ndikufuna kukuuza pamaso pa anthu onse. 8 Aneneri akalekale amene analipo ineyo ndisanakhalepo komanso iweyo usanakhalepo ankalosera za nkhondo, masoka ndi miliri yoti igwere* mayiko ambiri ndi maufumu amphamvu. 9 Ngati mneneri walosera zokhudza mtendere zinthuzo nʼkuchitikadi, mʼpamene zimadziwika kuti Yehova anamutumadi mneneriyo.”
10 Hananiya atamva zimenezo anatenga goli limene linali mʼkhosi mwa mneneri Yeremiya nʼkulithyola.+ 11 Kenako Hananiya anauza anthu onse amene anali pamenepo kuti: “Yehova wanena kuti, ‘Mofanana ndi mmene ndathyolera goli ili, zaka ziwiri zisanathe,+ ndidzathyola goli la Nebukadinezara mfumu ya Babulo limene waveka mitundu yonse ya anthu.’” Zitatero, mneneri Yeremiya anachokapo.
12 Mneneri Hananiya atathyola goli limene linali mʼkhosi mwa mneneri Yeremiya, Yehova anauza Yeremiya kuti: 13 “Pita ukauze Hananiya kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Iwe wathyola magoli amtengo+ koma mʼmalomwake padzakhala magoli achitsulo.” 14 Chifukwa Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti: “Ndidzaika magoli achitsulo pamakosi a mitundu ya anthu yonseyi kuti atumikire Nebukadinezara mfumu ya Babulo, ndipo akuyenera kudzamutumikira.+ Nebukadinezara ndidzamupatsanso ngakhale nyama zakutchire.”’”+
15 Kenako mneneri Yeremiya anauza mneneri Hananiya+ kuti: “Tamvera iwe Hananiya! Yehova sanakutume, koma iwe wachititsa anthuwa kukhulupirira zinthu zabodza.+ 16 Choncho Yehova wanena kuti, ‘Ndikukuchotsera moyo wako. Chaka chomwe chino iweyo ufa, chifukwa walimbikitsa anthu kuti apandukire Yehova.’”+
17 Choncho mneneri Hananiya anamwalira chaka chomwecho, mʼmwezi wa 7.
29 Awa ndi mawu amʼkalata imene mneneri Yeremiya anatumiza kuchokera ku Yerusalemu kupita kwa akuluakulu onse amene anali mʼgulu la anthu amene anali ku ukapolo, kwa ansembe, kwa aneneri ndi kwa anthu onse amene Nebukadinezara anawatenga ku Yerusalemu nʼkupita nawo ku ukapolo ku Babulo. 2 Analemba kalata imeneyi pambuyo poti Mfumu Yekoniya,+ mayi a mfumu,+ nduna zapanyumba ya mfumu, akalonga a Yuda ndi Yerusalemu, amisiri komanso anthu osula zitsulo* achoka ku Yerusalemu.+ 3 Yeremiya anatumiza kalatayi ku Babulo kudzera mwa Elasa mwana wa Safani+ ndi Gemariya mwana wa Hilikiya, amene Mfumu Zedekiya+ ya ku Yuda inawatuma kwa Mfumu Nebukadinezara ya ku Babulo. Kalatayo inali ndi mawu akuti:
4 “Kwa anthu onse amene anatengedwa kupita ku ukapolo, amene Mulungu anawachititsa kuti achoke ku Yerusalemu nʼkupita ku ukapolo ku Babulo, Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Mulungu wa Isiraeli akuti, 5 ‘Mangani nyumba nʼkumakhalamo. Limani minda nʼkumadya zipatso zake. 6 Tengani akazi ndipo mubereke ana aamuna ndi aakazi. Ana anu aamuna muwapezere akazi ndipo ana anu aakazi muwalole kuti akwatiwe kuti nawonso abereke ana aamuna ndi aakazi. Muchulukane kumeneko, musakhale ochepa ayi. 7 Ndipo mzinda umene ndakupititsani kuti mukakhale akapolo, muziufunira mtendere. Muziupempherera kwa Yehova chifukwa mzindawo ukakhala pa mtendere inunso mudzakhala pa mtendere.+ 8 Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Mulungu wa Isiraeli wanena kuti: “Musalole kuti aneneri anu komanso anthu ochita zamaula amene ali pakati panu akupusitseni+ ndipo musamvere maloto amene alota. 9 Chifukwa ‘akulosera zabodza kwa inu mʼdzina langa. Ine sindinawatume,’+ akutero Yehova.”’”
10 “Yehova wanena kuti, ‘Zaka 70 zikadzakwana muli ku Babulo, ndidzakusamalirani+ ndipo ndidzakwaniritsa lonjezo langa pokubwezeretsani kumalo ano.’+
11 ‘Ndikudziwa bwino zimene ndikuganiza zokhudza inu. Ndikuganiza zokupatsani mtendere osati masoka+ ndiponso zokupatsani tsogolo labwino ndi chiyembekezo chabwino,’ akutero Yehova.+ 12 ‘Mudzandiitana komanso mudzabwera nʼkupemphera kwa ine ndipo ine ndidzakumvetserani.’+
13 ‘Mudzandifunafuna ndipo mudzandipeza+ chifukwa mudzandifunafuna ndi mtima wanu wonse.+ 14 Ndidzakulolani kuti mundipeze,’+ akutero Yehova. ‘Ndidzasonkhanitsa anthu amene anagwidwa nʼkutengedwa kupita kumayiko ena kuchokera mʼmitundu yonse ndi kumalo onse kumene ndinakubalalitsirani,’+ akutero Yehova. ‘Kenako ndidzakubwezeretsani kumalo amene ndinakuchotsani pa nthawi imene ndinakupititsani ku ukapolo.’+
15 Koma inu mwanena kuti, ‘Yehova watiikira aneneri ku Babulo.’
16 Izi ndi zimene Yehova akunena kwa mfumu imene ikukhala pampando wachifumu wa Davide+ ndiponso kwa anthu onse amene akukhala mumzinda wa Yerusalemu, abale anu amene sanapite nanu ku ukapolo, 17 ‘Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti: “Ine ndikuwatumizira lupanga, njala ndi mliri*+ ndipo ndidzawachititsa kuti akhale ngati nkhuyu zowola* zimene ndi zoipa kwambiri moti munthu sangadye.”’+
18 ‘Ndidzawathamangitsa ndi lupanga,+ njala ndi mliri ndipo ndidzawapangitsa kuti akhale chinthu chochititsa mantha kwa maufumu onse apadziko lapansi.+ Komanso ndidzawachititsa kuti akhale chinthu chotembereredwa, chodabwitsa, chochiimbira mluzu+ ndiponso kuchinyoza pakati pa mitundu yonse ya anthu kumene ndidzawabalalitsireko.+ 19 Ndidzawachitira zimenezi chifukwa sanamvere mawu anga amene ndinawatumizira kudzera mwa atumiki anga omwe ndi aneneri, amene ndinkawatumiza mobwerezabwereza,’* akutero Yehova.+
‘Koma inu simunamvere,’+ akutero Yehova.
20 Choncho imvani mawu a Yehova, inu nonse amene muli ku ukapolo, amene ndinakuchotsani ku Yerusalemu nʼkukupititsani ku Babulo. 21 Ponena za Ahabu mwana wa Kolaya komanso Zedekiya mwana wa Maaseya, amene akulosera zabodza kwa inu mʼdzina langa,+ Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Anthu amenewa ndikuwapereka mʼmanja mwa Mfumu Nebukadinezara* ya ku Babulo ndipo adzawapha inu mukuona. 22 Ndipo zimene zidzawachitikire zidzakhala temberero limene anthu amene anatengedwa ku Yuda kupita ku ukapolo ku Babulo azidzanena kuti: “Yehova akuchititse kuti ukhale ngati Zedekiya ndi Ahabu amene mfumu ya Babulo inawawotcha pamoto!” 23 Chifukwa anachita zinthu zochititsa manyazi mu Isiraeli.+ Ankachita chigololo ndi akazi a anzawo komanso akulankhula zabodza mʼdzina langa zimene ine sindinawalamule.+
“Ine ndikuzidziwa zimenezi ndipo ndine mboni,”+ akutero Yehova.’”
24 “Ndiyeno Semaya+ wa ku Nehelamu ukamuuze kuti, 25 ‘Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Mulungu wa Isiraeli wanena kuti: “Chifukwa chakuti watumiza makalata mʼdzina lako kwa anthu onse amene ali ku Yerusalemu, kwa Zefaniya+ mwana wa Maaseya, amene ndi wansembe ndi kwa ansembe onse, onena kuti, 26 ‘Yehova wakuika kuti ukhale wansembe mʼmalo mwa Yehoyada wansembe, kuti ukhale woyangʼanira mʼnyumba ya Yehova komanso kuti uzimanga munthu aliyense wamisala, amene akuchita zinthu ngati mneneri ndipo uzimuika mʼmatangadza, miyendo, manja ndi mutu womwe.+ 27 Nanga nʼchifukwa chiyani sunalange Yeremiya wa ku Anatoti,+ amene akuchita zinthu ngati mneneri pamaso pako?+ 28 Iye watitumizira kalata kuno ku Babulo yonena kuti: “Mukhala akapolo kwa nthawi yaitali. Mangani nyumba nʼkumakhalamo. Limani minda nʼkumadya zipatso zake,+ . . .”’”’”
29 Zefaniya+ wansembe atawerengera mneneri Yeremiya kalata imeneyi, 30 Yehova anauza Yeremiya kuti: 31 “Anthu onse amene ali ku ukapolo uwatumizire uthenga wakuti, ‘Ponena za Semaya wa ku Nehelamu, Yehova wanena kuti: “Popeza Semaya analosera kwa inu, ngakhale kuti ine sindinamutume ndipo anayesetsa kukuchititsani kuti mukhulupirire zinthu zabodza,+ 32 Yehova wanena kuti, ‘Ine ndilanga Semaya wa ku Nehelamu ndi mbadwa zake. Sipadzapezeka mwamuna aliyense wochokera mʼbanja lake amene adzapulumuke pakati pa anthu awa. Ndipo iye sadzaona zabwino zimene ndidzachitire anthu anga chifukwa walimbikitsa anthu kuti apandukire Yehova,’ akutero Yehova.”’”
30 Mawu amene Yehova anauza Yeremiya ndi awa: 2 “Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Lemba mʼbuku mawu onse amene ndikukuuza. 3 “Taona! masiku akubwera,” akutero Yehova, “pamene ndidzasonkhanitsa Isiraeli ndi Yuda,+ anthu anga amene anagwidwa nʼkutengedwa kupita kudziko lina,” akutero Yehova. “Iwo ndidzawabwezeretsa kudziko limene ndinapatsa makolo awo ndipo adzalitenga kuti likhalenso lawo.”’”+
4 Awa ndi mawu amene Yehova anauza Isiraeli ndi Yuda.
5 Yehova wanena kuti:
“Ife tamva phokoso la anthu amene akunjenjemera.
Iwo agwidwa ndi mantha ndipo palibe mtendere.
6 Tafunsani, kodi mwamuna angabereke mwana?
Nanga nʼchifukwa chiyani ndikuona mwamuna aliyense wamphamvu atagwira manja pamimba* pake
Ngati mkazi amene akubereka?+
Nʼchifukwa chiyani aliyense nkhope yake yafooka?
7 Mayo ine! Chifukwa tsiku limenelo lidzakhala lochititsa mantha.*+
Ndipo palibe lofanana nalo.
Tsiku limenelo lidzakhala lamavuto kwa Yakobo.
Koma adzapulumutsidwa mʼmavuto amenewa.
8 Pa tsiku limenelo ndidzathyola goli limene lili mʼkhosi lanu. Ndidzadula pakati zingwe zimene akumangani nazo, moti anthu achilendo sadzachititsanso kuti Yakobo akhale kapolo wawo,” akutero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba. 9 “Inu mudzatumikira Yehova Mulungu wanu ndi Davide mfumu yanu imene ndidzakupatseni.+
10 Koma iwe Yakobo mtumiki wanga usachite mantha,” akutero Yehova,
“Ndipo iwe Isiraeli usaope.+
Chifukwa ndidzakupulumutsa kuchokera kutali
Ndidzapulumutsanso ana ako kuchokera kudziko limene anatengedwa kukakhala akapolo.+
Yakobo adzabwerera ndipo adzakhala mosatekeseka komanso mopanda zosokoneza.
Sipadzakhala wowaopseza.+
11 Chifukwa ine ndili ndi iwe kuti ndikupulumutse,” akutero Yehova.
12 Yehova wanena kuti:
“Kuwonongeka kwako ndi kosachiritsika.+
Ndiponso bala lako ndi losachiritsika.
13 Palibe woti akuchonderere pa mlandu wako.
Palibe njira iliyonse yochiritsira bala lako.
Ndipo palibe mankhwala amene angakuchiritse.
14 Onse amene ankakukonda kwambiri akuiwala.+
Iwo sakukufunafunanso.
Ndakumenya ngati mmene angakumenyere mdani,+
Ndipo ndakulanga ngati mmene angakulangire munthu wankhanza,
Chifukwa cha kulakwa kwako kwakukulu ndi kuchuluka kwa machimo ako.+
15 Kodi pali chifukwa choti udandaulire ndi chilango chimene wapatsidwa?
Ululu wako ndi wosachiritsika.
Chifukwa cha kulakwa kwako kwakukulu ndi kuchuluka kwa machimo ako,+
Ine ndakuchitira zimenezi.
16 Choncho onse okuwononga adzawonongedwa,+
Ndipo adani ako onse nawonso adzatengedwa kupita ku ukapolo.+
Amene akulanda katundu wako nawonso adzalandidwa katundu wawo.
Ndipo anthu onse amene akulanda zinthu zako ndidzawapereka mʼmanja mwa olanda zinthu.+
17 Ndidzakuchititsa kuti ukhalenso wathanzi ndipo ndidzapoletsa mabala ako,”+ akutero Yehova.
“Ngakhale kuti anakana kukulandira ndipo anakutchula kuti:
‘Ziyoni amene palibe amene akumufunafuna.’”+
18 Yehova wanena kuti:
“Ndikusonkhanitsa anthu amʼmatenti a Yakobo amene anagwidwa nʼkutengedwa kupita kudziko lina,+
Ndipo ndidzamvera chisoni malo okhala a Yakobo.
Mzinda udzamangidwanso pamalo amene unali poyamba,+
Ndipo nsanja yokhala ndi mpanda wolimba idzakhala pamalo ake oyenerera.
19 Kwa iwo kudzamveka mawu oyamikira ndi phokoso la kuseka kwa anthu.+
Ndidzawachulukitsa moti sadzakhala ochepa.+
Ndidzawachititsa kuti akhale ambiri,*
Ndipo sadzakhala anthu ochepa.+
20 Ana ake aamuna zinthu zidzawayendera bwino ngati mmene zinalili poyamba,
Ndipo ndidzawapangitsa kuti akhale anthu amphamvu pamaso panga.+
Ndidzalanga anthu onse amene amamupondereza.+
21 Mtsogoleri wake adzachokera pakati pa anthu ake,
Ndipo wolamulira wake adzachokera pakati pa mbadwa zake.
Ndidzamulola kuti andiyandikire ndipo adzabwera kwa ine.
Chifukwa ndi ndani amene angalimbe mtima kuti andiyandikire?” akutero Yehova.
22 “Inu mudzakhala anthu anga+ ndipo ine ndidzakhala Mulungu wanu.”+
23 Taonani! Mkwiyo wa Yehova udzawomba ngati mphepo yamkuntho,+
Udzawomba ngati kamvulumvulu wamphamvu pamitu ya anthu oipa.
24 Mkwiyo woyaka moto wa Yehova sudzabwerera
Mpaka atachita komanso kukwaniritsa zofuna za mtima wake.+
Mʼmasiku otsiriza, mudzamvetsa zimenezi.+
31 “Pa nthawi imeneyo ndidzakhala Mulungu wa mabanja onse a Isiraeli ndipo iwo adzakhala anthu anga,” akutero Yehova.+
2 Yehova wanena kuti:
“Anthu amene anapulumuka ku lupanga, ndinawakomera mtima mʼchipululu,
Pamene Isiraeli ankapita kumalo ake opumulirako.”
3 Yehova anaonekera kwa ine ali kutali ndipo anati:
“Ine ndakukonda ndipo ndidzakukonda mpaka kalekale.
Nʼchifukwa chake ndakukokera kwa ine ndi chikondi chokhulupirika.*+
4 Choncho ndidzakumanganso ndipo udzakhalanso mtundu,+
6 Chifukwa tsiku lidzafika limene alonda amene ali mʼmapiri a Efuraimu adzafuula kuti:
‘Nyamukani, tiyeni tipite ku Ziyoni kwa Yehova Mulungu wathu.’”+
7 Yehova wanena kuti:
“Fuulirani Yakobo mosangalala,
Fuulani mosangalala chifukwa muli patsogolo pa mitundu ina.+
Lengezani zimenezi. Tamandani Mulungu nʼkunena kuti,
‘Inu Yehova pulumutsani anthu anu, otsalira a Isiraeli.’+
8 Ine ndikuwabweretsa kuchokera kudziko lakumpoto,+
Ndidzawasonkhanitsa pamodzi kuchokera kumalekezero a dziko lapansi.+
Pakati pawo padzakhala anthu amene ali ndi vuto losaona, olumala,+
Azimayi oyembekezera komanso amene atsala pangʼono kubereka,
Onse pamodzi adzabwerera kuno ali chigulu.+
9 Iwo adzabwera akulira.+
Ndidzawatsogolera akadzandipempha kuti ndiwakomere mtima.
Chifukwa ine ndine Bambo ake a Isiraeli ndipo Efuraimu ndi mwana wanga woyamba kubadwa.”+
10 Inu mitundu ya anthu, imvani mawu a Yehova,
Ndipo mulengeze mawuwo kuzilumba zakutali kuti:+
“Amene anabalalitsa Aisiraeli ndi amene adzawasonkhanitse.
Adzawayangʼanira ngati mmene mʼbusa amachitira ndi nkhosa zake.+
11 Chifukwa Yehova adzawombola Yakobo+
Ndipo adzamupulumutsa mʼmanja mwa munthu wamphamvu kuposa iyeyo.+
12 Iwo adzabwera nʼkufuula mosangalala pamwamba pa phiri la Ziyoni.+
Nkhope zawo zidzawala chifukwa cha ubwino wa* Yehova.
Chifukwa cha mbewu, vinyo watsopano+ ndi mafuta,
Ndiponso chifukwa cha ana a nkhosa ndi ana a ngʼombe.+
13 “Pa nthawi imeneyo, anamwali,
Anyamata ndiponso amuna achikulire, adzavina pamodzi mosangalala.+
Kulira kwawo ndidzakusandutsa chisangalalo.+
Ndidzawatonthoza ndipo ndidzachititsa kuti akhale osangalala mʼmalo mokhala achisoni.+
14 Ansembe ndidzawapatsa chakudya chochuluka,*
Ndipo anthu anga adzakhutira ndi zinthu zabwino zimene ndidzawapatse,”+ akutero Yehova.
15 “Yehova wanena kuti:
‘Mawu amveka ku Rama.+ Kwamveka kulira mofuula ndiponso komvetsa chisoni.
Rakele akulirira ana ake.+
Iye wakana kutonthozedwa pamene akulirira ana ake,
Chifukwa ana akewo kulibenso.’”+
16 Yehova wanena kuti:
“‘Tonthola, usalire ndipo usagwetsenso misozi,
Chifukwa ulandira mphoto pa ntchito yako,’ akutero Yehova.
‘Ana ako adzabwerera kuchokera kudziko la mdani.’+
17 ‘Uli ndi tsogolo labwino,+
Ndipo ana ako adzabwerera kudziko lawo,’ akutero Yehova.”+
18 “Ndamva Efuraimu akulira kuti,
‘Ndinali ngati mwana wa ngʼombe wosaphunzitsidwa,
Mwandidzudzula ndipo ndaphunzirapo kanthu.
Ndithandizeni kuti ndibwerere ndipo ndidzabwereradi,
Chifukwa inu ndinu Yehova Mulungu wanga.
19 Nditabwerera kwa inu ndinadzimvera chisoni.+
Mutandithandiza kuzindikira, ndinadzimenya pantchafu chifukwa cha chisoni.
Ndinachita manyazi ndipo ndinaoneka wonyozeka,+
Chifukwa cha zinthu zimene ndinachita ndili wachinyamata.’”
20 “Kodi Efuraimu si mwana wanga wamtengo wapatali, amene ndimamukonda?+
Ngakhale kuti nthawi zambiri ndimamudzudzula, ndimamukonda ndipo ndimamukumbukirabe.
Nʼchifukwa chake ndakhudzika naye* kwambiri.+
Ndipo sindidzalephera kumumvera chisoni,” akutero Yehova.+
21 “Udziikire zizindikiro zamumsewu,
Ndipo udziikire zikwangwani.+
Maganizo ako akhale panjirayo, njira imene ukuyenera kuyendamo.+
Bwerera iwe namwali wa Isiraeli. Bwerera kumizinda yakoyi.
22 Kodi udzapita uku ndi uku mpaka liti, iwe mwana wamkazi wosakhulupirika?
Chifukwa Yehova walenga chinthu chatsopano padziko lapansi.
Chinthucho nʼchakuti, mkazi adzafunafuna mwakhama mwamuna wake.”
23 Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti: “Ndikadzasonkhanitsa anthu a mtundu wawo amene anagwidwa nʼkutengedwa kupita kudziko lina, iwo adzanenanso mawu awa mʼdziko la Yuda ndi mʼmizinda yake kuti, ‘Yehova akudalitse iwe malo olungama okhalamo,+ iwe phiri lopatulika.’+ 24 Anthu okhala mʼmizinda, alimi komanso abusa a ziweto azidzakhala limodzi ku Yuda.+ 25 Chifukwa ndidzapereka mphamvu kwa munthu wotopa ndipo ndidzalimbikitsa aliyense amene wafooka.”+
26 Kenako ndinadzidzimuka nʼkutsegula maso anga. Ndinali nditagona tulo tokoma.
27 “Taonani! Masiku akubwera, pamene ndidzachititsa kuti nyumba ya Isiraeli ndi nyumba ya Yuda ikhalenso ndi anthu ochuluka komanso ziweto zambiri,” akutero Yehova.+
28 “Ndinkawayangʼanitsitsa kuti ndiwazule, ndiwagwetse, ndiwapasule, ndiwawononge komanso kuti ndiwasakaze.+ Mofanana ndi zimenezi, ndidzawayangʼanitsitsanso kuti ndiwamange komanso ndiwadzale,”+ akutero Yehova. 29 “Masiku amenewo sadzanenanso kuti, ‘Abambo anadya mphesa zosapsa koma mano a ana awo ndi amene anayezimira.’*+ 30 Komatu munthu aliyense adzafa chifukwa cha zolakwa zake. Mano a munthu aliyense amene wadya mphesa zosapsa ndi amene adzayezimire.”
31 “Taonani! Masiku akubwera, pamene ndidzachita pangano latsopano ndi nyumba ya Isiraeli komanso nyumba ya Yuda,” akutero Yehova.+ 32 “Koma silidzakhala pangano lofanana ndi limene ndinachita ndi makolo awo, pa tsiku limene ndinagwira dzanja lawo kuti ndiwatulutse mʼdziko la Iguputo.+ ‘Pangano langa limenelo analiphwanya+ ngakhale kuti ine ndinali mbuye wawo* weniweni,’ akutero Yehova.”
33 “Pangano limene ndidzapangane ndi nyumba ya Isiraeli pambuyo pa masiku amenewo ndi ili: Ndidzaika chilamulo changa mwa iwo+ ndipo ndidzachilemba mumtima mwawo.+ Ine ndidzakhala Mulungu wawo ndipo iwo adzakhala anthu anga,” akutero Yehova.+
34 “Munthu sadzaphunzitsanso mnzake kapena mʼbale wake kuti, ‘Mumʼdziwe Yehova!’+ chifukwa aliyense adzandidziwa kuyambira wamngʼono mpaka wamkulu,”+ akutero Yehova. “Ine ndidzawakhululukira zolakwa zawo ndipo machimo awo sindidzawakumbukiranso.”+
35 Yehova amene amapereka dzuwa kuti liziwala masana,
Amene amaika malamulo oti mwezi ndi nyenyezi ziziwala usiku,
Amene amavundula nyanja
Kuti mafunde ake achite phokoso,
Amene dzina lake ndi Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, wanena kuti:+
36 “‘Ngati malamulo amenewa angalephere kugwira ntchito yake,
Ndiye kutinso mbadwa za Isiraeli zingasiye kukhala mtundu, umene umakhala pamaso panga nthawi zonse,’ akutero Yehova.”+
37 Yehova wanena kuti: “‘Ngati kumwamba kungayezedwe ndipo ngati maziko a dziko lapansi angafufuzidwe, ndiye kuti inenso ndingakane mbadwa zonse za Isiraeli chifukwa cha zonse zimene achita,’ akutero Yehova.”+
38 “Taonani! Masiku akubwera,” akutero Yehova, “pamene anthu adzamangira Yehova mzinda+ kuyambira pa Nsanja ya Hananeli+ mpaka ku Geti la Pakona.+ 39 Ndipo chingwe choyezera+ chidzachokera kumeneko nʼkukafika kuphiri la Garebi, kenako chidzakhotera ku Gowa. 40 Chigwa chonse cha mitembo ndi cha phulusa,* masitepe onse mpaka kukafika kuchigwa cha Kidironi,+ mpaka kukona ya Geti la Hatchi+ chakumʼmawa, zidzakhala zoyera kwa Yehova.+ Mzindawu sudzazulidwa ndipo sudzagwetsedwanso.”
32 Awa ndi mawu amene Yehova anauza Yeremiya mʼchaka cha 10 cha ulamuliro wa Zedekiya mfumu ya Yuda. Chimenechi chinali chaka cha 18 cha Nebukadinezara.*+ 2 Pa nthawi imeneyo, asilikali a mfumu ya Babulo anali atazungulira Yerusalemu. Ndipo mneneri Yeremiya anali atamutsekera mʼnyumba imene inali mʼBwalo la Alonda,+ limene linali pafupi ndi nyumba ya mfumu ya Yuda. 3 Mfumu Zedekiya ya Yuda inamutsekera+ kumeneko nʼkunena kuti: “Nʼchifukwa chiyani ukulosera zimenezi? Ukunena kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Mzindawu ndidzaupereka mʼmanja mwa mfumu ya Babulo ndipo idzaulanda,+ 4 ndipo Zedekiya mfumu ya Yuda sadzapulumuka mʼmanja mwa Akasidi, chifukwa adzaperekedwa ndithu mʼmanja mwa mfumu ya Babulo ndipo idzalankhulana ndi kuonana naye maso ndi maso.”’+ 5 ‘Mfumuyo idzatenga Zedekiya kupita naye ku Babulo ndipo adzakhala komweko mpaka nditasankha zoti ndimuchite,’ akutero Yehova. ‘Ngakhale kuti mukupitiriza kumenyana ndi Akasidi simudzapambana.’”+
6 Ndiyeno Yeremiya anati: “Yehova wandiuza kuti, 7 ‘Kukubwera Hanameli mwana wa Salumu mʼbale wawo wa bambo ako, kudzakuuza kuti: “Ugule munda wanga wa ku Anatoti+ chifukwa munthu woyamba amene ali ndi ufulu wogula mundawo ndi iweyo.”’”+
8 Ndiyeno Hanameli mwana wa mʼbale wawo wa bambo anga anandipeza mʼBwalo la Alonda mogwirizana ndi zimene Yehova ananena. Iye anandiuza kuti: “Gula munda wanga wa ku Anatoti, umene uli mʼdziko la Benjamini, chifukwa iweyo ndi amene uli ndi ufulu wouwombola nʼkuutenga kuti ukhale cholowa chako. Uugule kuti ukhale wako.” Atatero ndinazindikira kuti mawu amenewa anali a Yehova.
9 Choncho ndinagula munda wa Hanameli mwana wa mʼbale wawo wa bambo anga umene unali ku Anatoti. Ndinamuyezera ndalama+ zake ndipo zinakwana masekeli* 7 ndi ndalama zina 10 zasiliva. 10 Kenako ndinalemba kalata ya pangano+ nʼkuikapo chidindo ndipo ndinaitana mboni+ kuti zidzasainire kalatayo. Ndiyeno ndinamuyezera ndalamazo pasikelo. 11 Ndiye mogwirizana ndi malamulo ndinatenga makalata onse a pangano, yomata ndi yosamata yomwe. 12 Kenako ndinapereka makalata a pangano ogulira mundawo kwa Baruki+ mwana wa Neriya,+ mwana wa Maseya. Ndinapereka makalatawo pamaso pa Hanameli mwana wa mʼbale wawo wa bambo anga, pamaso pa mboni zimene zinasaina makalatawo ndi pamaso pa Ayuda onse amene anali mʼBwalo la Alonda.+
13 Ndiyeno ndinalamula Baruki anthu onsewo akumva kuti: 14 “Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Tenga makalata awa, makalata a pangano ogulira mundawa, kalata yomata ndi kalata yosamatayo ndipo uwaike mʼmbiya kuti akhale kwa nthawi yaitali.’ 15 Chifukwa Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Mʼdziko lino anthu adzagulanso nyumba, minda ndi minda ya mpesa.’”+
16 Nditapereka makalata amenewa kwa Baruki mwana wa Neriya, ndinapemphera kwa Yehova kuti: 17 “Inu Yehova Ambuye Wamkulu Koposa. Inuyo ndi amene munapanga kumwamba ndi dziko lapansi pogwiritsa ntchito mphamvu zanu zazikulu+ ndi dzanja lanu lotambasula. Palibe chimene chingakuvuteni. 18 Inu amene mumasonyeza anthu masauzande ambiri chikondi chokhulupirika koma mumabwezera kwa ana,* zolakwa za abambo awo.+ Inu ndinu Mulungu woona, wamkulu ndi wamphamvu ndipo dzina lanu ndinu Yehova wa magulu ankhondo akumwamba. 19 Zolinga zanu ndi zazikulu ndipo zochita zanu ndi zamphamvu.+ Maso anu amaona zonse zimene anthu amachita,+ kuti munthu aliyense mumuchitire zinthu mogwirizana ndi njira zake komanso zochita zake.+ 20 Inu munachita zizindikiro ndi zodabwitsa mʼdziko la Iguputo zimene zikudziwikabe mpaka lero. Ndipo zimenezo zinachititsa kuti dzina lanu lidziwike mu Isiraeli komanso pakati pa anthu onse+ ngati mmene likudziwikira lero. 21 Inu munatulutsa anthu anu Aisiraeli mʼdziko la Iguputo pogwiritsa ntchito zizindikiro, zodabwitsa, dzanja lamphamvu, mkono wotambasula ndi zinthu zochititsa mantha kwambiri.+
22 Patapita nthawi munawapatsa dziko lino limene munalumbira kuti mudzalipereka kwa makolo awo,+ lomwe ndi dziko loyenda mkaka ndi uchi.+ 23 Iwo analowa mʼdzikoli nʼkulitenga kuti likhale lawo, koma sanamvere mawu anu kapena kuyenda motsatira malamulo anu. Iwo sanachite zinthu zonse zimene munawalamula kuti achite, nʼchifukwa chake munawagwetsera masoka onsewa.+ 24 Taonani! Anthu abwera kumzinda uno ndipo amanga malo okwera omenyerapo nkhondo kuti aulande,+ moti uperekedwa mʼmanja mwa Akasidi amene akumenyana ndi anthu amumzindawu. Anthu adzafa ndi lupanga,+ njala ndi mliri.*+ Zinthu zonse zimene munanena zachitika ndipo ndi izi mukuzionazi. 25 Koma inu Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, mwandiuza kuti, ‘Gula mundawu ndi ndalama pamaso pa mboni,’ ngakhale kuti mzindawu uperekedwa ndithu mʼmanja mwa Akasidi.”
26 Zitatero Yehova anauza Yeremiya kuti: 27 “Ine ndine Yehova, Mulungu wa anthu onse. Kodi pali chinthu chovuta kwa ine? 28 Choncho Yehova wanena kuti, ‘Tsopano ndikupereka mzindawu mʼmanja mwa Akasidi ndi mʼmanja mwa Nebukadinezara* mfumu ya Babulo, ndipo aulanda.+ 29 Akasidi amene akumenyana ndi anthu amumzindawu adzabwera nʼkuyatsa mzindawu moti udzapseratu.+ Adzawotchanso nyumba zimene pamadenga ake anthu ankaperekerapo nsembe kwa Baala komanso nsembe zachakumwa kwa milungu ina kuti andikhumudwitse.’+
30 ‘Aisiraeli ndi Ayuda akhala akuchita zoipa zokhazokha pamaso panga kuyambira ali ana.+ Aisiraeli akhala akundikhumudwitsa ndi ntchito za manja awo,’ akutero Yehova. 31 ‘Mzinda uwu wakhala chinthu chimene chimandikwiyitsa komanso kundipsetsa mtima kungoyambira pamene unamangidwa mpaka lero.+ Choncho ukuyenera kuchotsedwa pamaso panga+ 32 chifukwa cha zoipa zonse zimene Aisiraeli ndi Ayuda achita nʼkundikhumudwitsa nazo. Achita zimenezi pamodzi ndi mafumu awo,+ akalonga awo,+ ansembe awo, aneneri awo,+ anthu a ku Yuda ndi anthu onse amene akukhala mu Yerusalemu. 33 Iwo anapitiriza kundifulatira ndipo sanandiyangʼane.+ Ngakhale kuti ndinayesetsa kuwaphunzitsa mobwerezabwereza,* palibe ngakhale mmodzi wa iwo amene anamvetsera kuti alandire malangizo.+ 34 Iwo anaika mafano awo onyansa mʼnyumba imene imatchedwa ndi dzina langa kuti aiipitse.+ 35 Kuwonjezera pamenepo, anamangira Baala malo okwera mʼChigwa cha Mwana wa Hinomu*+ kuti aziwotcha* ana awo aamuna ndi ana awo aakazi pamoto ngati nsembe kwa Moleki.+ Ine sindinawalamule+ kuti azichita zimenezi. Ndipo sindinaganizirepo mumtima mwanga* zowauza kuti achite chinthu chonyansa chimenechi, chimene chachititsa kuti Yuda achimwe.’
36 Choncho ponena za mzinda uwu umene mukunena kuti uperekedwa mʼmanja mwa mfumu ya Babulo kuti uwonongedwe ndi lupanga, njala ndi mliri, Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, 37 ‘Ine ndidzawasonkhanitsa pamodzi kuchokera kumayiko onse kumene ndinawabalalitsira nditakwiya, kupsa mtima ndiponso ndili ndi ukali waukulu.+ Ndidzawabwezeretsa mʼdziko lino nʼkuwachititsa kuti azikhala motetezeka.+ 38 Iwo adzakhala anthu anga ndipo ine ndidzakhala Mulungu wawo.+ 39 Ndidzawapatsa mtima umodzi+ komanso kuwachititsa kuti aziyenda mʼnjira imodzi kuti azindiopa nthawi zonse. Ndidzachita zimenezi kuti iwo limodzi ndi ana awo zinthu ziziwayendera bwino.+ 40 Ndidzachita nawo pangano+ lomwe lidzakhalapo mpaka kalekale. Panganoli lidzakhala lakuti sindidzasiya kuwachitira zinthu zabwino+ ndipo ndidzawapatsa mtima woti azindiopa kuti asachoke kwa ine.+ 41 Ndidzasangalala nawo ndipo ndidzawachitira zabwino.+ Ndidzawachititsa kuti azikhala mʼdziko lino+ mpaka kalekale. Ndidzachita zimenezi ndi mtima wanga wonse komanso moyo wanga wonse.’”
42 “Yehova wanena kuti, ‘Mofanana ndi mmene ndabweretsera anthu awa masoka aakulu onsewa, ndidzawabweretseranso zinthu zabwino zonse zimene ndikuwalonjezazi.+ 43 Anthu adzagulanso minda mʼdziko lino,+ ngakhale mukunena kuti: “Dziko ili ndi bwinja, lopanda munthu wokhalamo kapena nyama yakutchire ndipo laperekedwa kwa Akasidi.”’
44 ‘Anthu adzagula minda ndi ndalama ndipo adzalemberana makalata a pangano pamaso pa mboni ndi kumata makalatawo. Zimenezi zidzachitika mʼdziko la Benjamini,+ mʼmadera ozungulira Yerusalemu, mʼmizinda ya Yuda,+ mʼmizinda yamʼmadera amapiri, mʼmizinda yamʼchigwa ndi mʼmizinda yakumʼmwera.+ Zidzakhala choncho chifukwa ndidzabwezeretsa anthu ake amene anatengedwa kupita kudziko lina,’+ akutero Yehova.”
33 Yeremiya adakali mʼBwalo la Alonda+ momwe anamutsekera, Yehova analankhula naye kachiwiri kuti: 2 “Yehova amene anapanga dziko lapansi, Yehova amene anawumba dzikoli nʼkulikhazikitsa mwamphamvu, Mulungu amene dzina lake ndi Yehova, wanena kuti, 3 ‘Mundiitane ndipo ndidzakuyankhani. Nthawi yomweyo ndidzakuuzani zinthu zazikulu ndi zovuta kuzimvetsa zimene simukuzidziwa.’”+
4 “Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena mawu okhudza nyumba zamumzinda uwu ndiponso okhudza nyumba za mafumu a Yuda, zimene zagwetsedwa chifukwa cha malo okwera omenyerapo nkhondo ndiponso lupanga la adani.+ 5 Wanenanso mawu okhudza anthu amene akubwera kudzamenyana ndi Akasidi komanso zokhudza malo amene adzaza ndi mitembo ya anthu amene ndawapha chifukwa cha mkwiyo wanga waukulu, omwe kuipa kwawo kwachititsa kuti mzindawu ndiubisire nkhope yanga. Iye wanena kuti: 6 ‘Ine ndichiritsa anthu amumzindawu nʼkuwapatsa thanzi labwino.+ Ndiwachiritsa nʼkuwapatsa mtendere wambiri ndi choonadi chochuluka.+ 7 Anthu a mu Yuda ndi a mu Isiraeli amene anatengedwa kupita kudziko lina ndidzawabwezeretsa+ ndipo adzakhalanso ngati mmene analili poyamba.+ 8 Ndidzawayeretsa ku zolakwa zonse zimene anandichimwira+ ndipo ndidzawakhululukira zolakwa zawo zonse zimene anandichimwira nʼkuphwanya nazo malamulo anga.+ 9 Mzindawu udzakhala ndi dzina limene lidzandisangalatse, udzachititsa kuti nditamandidwe ndiponso kulandira ulemerero pakati pa mitundu yonse yapadziko lapansi, imene idzamve za zinthu zabwino zimene ndinachitira anthu anga.+ Anthu a mitundu inawo adzachita mantha ndipo adzanjenjemera+ chifukwa cha zinthu zonse zabwino komanso mtendere umene ndidzabweretse pa mzindawu.’”+
10 “Yehova wanena kuti: ‘Pamalo ano amene mudzanene kuti ndi bwinja, opanda anthu kapena ziweto, mʼmizinda ya Yuda ndi mʼmisewu ya Yerusalemu imene yawonongeka, moti mulibe anthu ndipo simukukhala aliyense ngakhale ziweto, mʼmalo amenewa mudzamveka 11 phokoso la chikondwerero ndi chisangalalo.+ Mudzamvekanso mawu a mkwati ndi mawu a mkwatibwi komanso mawu a anthu amene akunena kuti: “Yamikani Yehova wa magulu ankhondo akumwamba chifukwa Yehova ndi wabwino+ ndipo chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale!”’+
‘Anthuwo adzabweretsa nsembe zoyamikira kunyumba ya Yehova,+ chifukwa ndidzabwezeretsa anthu amʼdzikoli, amene anatengedwa kupita kudziko lina, kuti akhalenso ngati mmene analili poyamba,’ akutero Yehova.”
12 “Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti: ‘Mʼdziko labwinja lino, lopanda anthu kapena ziweto komanso mʼmizinda yake yonse, mudzakhalanso malo odyetserako ziweto kumene abusa azidzapumitsirako ziweto zawo.’+
13 ‘Mʼmizinda yamʼmadera amapiri, mʼmizinda yamʼchigwa, mʼmizinda yakumʼmwera, mʼdziko la Benjamini, mʼmadera ozungulira Yerusalemu+ ndi mʼmizinda ya Yuda,+ ziweto zidzadutsanso pansi pa dzanja la munthu amene akuziwerenga,’ akutero Yehova.”
14 “‘Taonani! Masiku akubwera pamene ndidzakwaniritsa lonjezo langa labwino lokhudza nyumba ya Isiraeli ndi nyumba ya Yuda,’ akutero Yehova.+ 15 ‘Mʼmasiku amenewo ndiponso nthawi imeneyo ndidzameretsera Davide mphukira+ yolungama* ndipo mphukirayo idzaweruza mwachilungamo mʼdzikoli.+ 16 Mʼmasiku amenewo Yuda adzapulumutsidwa+ ndipo Yerusalemu adzakhala mwamtendere.+ Yerusalemu azidzatchulidwa kuti, Yehova Ndi Chilungamo Chathu.’”+
17 “Yehova wanena kuti, ‘Mʼnyumba ya Davide simudzalephera kupezeka munthu woti akhale pampando wachifumu wa nyumba ya Isiraeli.+ 18 Ndipo pakati pa Alevi omwe ndi ansembe sipadzalephera kupezeka mwamuna wonditumikira woti azipereka nsembe zopsereza zathunthu, nsembe zambewu komanso nsembe zina.’”
19 Yehova analankhulanso ndi Yeremiya kuti: 20 “Yehova wanena kuti, ‘Ngati anthu inu mungathe kuphwanya pangano langa loti kukhale masana ndi pangano langa loti kukhale usiku, kuti masana ndi usiku zisafike pa nthawi yake,+ 21 ndiye kuti inenso ndingathe kuphwanya pangano langa ndi Davide mtumiki wanga+ kuti asakhale ndi mwana woti adzalamulire monga mfumu pampando wake wachifumu wa Davide.+ Ndingachitenso chimodzimodzi ndi pangano langa ndi atumiki anga Alevi omwe ndi ansembe.+ 22 Ine ndidzachulukitsa mbadwa* za Davide mtumiki wanga ndi Alevi amene akunditumikira. Ndidzazichulukitsa mofanana ndi kuchuluka kwa nyenyezi zonse zakumwamba* zimene sizingawerengedwe ndiponso mofanana ndi mchenga umene sungayezedwe.’”
23 Kenako Yehova analankhulanso ndi Yeremiya kuti: 24 “Kodi sunamve zimene anthu awa akunena kuti, ‘Mabanja awiri amene Yehova anawasankha, adzawakanansoʼ? Adani akuchitira anthu anga zinthu zopanda ulemu ndipo sakuwaonanso ngati mtundu wa anthu.
25 Yehova wanena kuti, ‘Mofanana ndi mmene ndinakhazikitsira pangano langa loti kukhale masana ndi usiku,+ malamulo akumwamba ndi dziko lapansi,+ 26 sindidzakananso mbadwa* za Yakobo ndi za Davide mtumiki wanga, kuti pakati pa mbadwa* zake ndisatengepo olamulira ana a Abulahamu,* Isaki ndi Yakobo. Chifukwa ndidzasonkhanitsa anthu onse amene anatengedwa kupita kudziko lina+ ndipo ndidzawamvera chisoni.’”+
34 Yehova analankhula ndi Yeremiya pamene Nebukadinezara* mfumu ya Babulo, asilikali ake onse, maufumu onse apadziko lapansi amene anali pansi pa ulamuliro wake ndiponso mitundu yonse ya anthu ankamenyana ndi Yerusalemu komanso mizinda yake yonse. Iye anati:+
2 “Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Pita ukauze Mfumu Zedekiya+ ya Yuda kuti: “Yehova wanena kuti, ‘Ine ndikupereka mzindawu mʼmanja mwa mfumu ya Babulo ndipo idzauwotcha ndi moto.+ 3 Iweyo adzakugwira ndithu nʼkukupereka kwa iye ndipo sudzathawa mʼmanja mwake.+ Udzaonana ndi mfumu ya Babulo maso ndi maso ndipo idzalankhula nawe. Iweyo udzapita ku Babulo.’+ 4 Koma iwe Zedekiya mfumu ya Yuda, imva mawu a Yehova akuti, ‘Ponena za iwe, Yehova wanena kuti: “Sudzafa ndi lupanga. 5 Udzafa mu mtendere.+ Anthu adzakuchitira mwambo wowotcha zinthu zonunkhira ngati mmene anachitira ndi makolo ako, mafumu amene analipo iwe usanabadwe. Polira maliro ako adzanena kuti, ‘Mayo ine mbuyanga!’ chifukwa ‘Ine ndalankhula mawu amenewa,’ akutero Yehova.”’”’”
6 Kenako mneneri Yeremiya anauza Mfumu Zedekiya ya Yuda mawu onsewa ku Yerusalemu, 7 pamene asilikali a mfumu ya Babulo ankamenyana ndi Yerusalemu komanso mizinda yonse ya mu Yuda imene inatsala,+ kuphatikizapo Lakisi+ ndi Azeka.+ Imeneyi ndi mizinda yokhayo ya mipanda yolimba kwambiri imene inatsala mu Yuda.
8 Yehova analankhula ndi Yeremiya pambuyo poti Mfumu Zedekiya yachita pangano ndi anthu onse a mu Yerusalemu kuti alengeze ufulu,+ 9 kuti aliyense amasule akapolo ake a Chiheberi, aamuna ndi aakazi, kuti pasapezeke munthu amene akusunga Myuda mnzake ngati kapolo wake. 10 Choncho akalonga onse ndi anthu onse anamvera. Iwo anachita pangano kuti aliyense amasule akapolo ake aamuna ndi aakazi kuti asakhalenso akapolo. Iwo anamvera nʼkuwalola kuti achoke. 11 Koma patapita nthawi, iwo anakatenganso akapolo aamuna ndi aakazi amene anawamasula aja ndipo anawakakamiza kuti akhalenso akapolo awo. 12 Choncho Yehova anauza Yeremiya mawu ndipo Yehova anati:
13 “Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Ine ndinachita pangano ndi makolo anu+ pa tsiku limene ndinawatulutsa mʼdziko la Iguputo, kumene anali akapolo.+ Ndinapangana nawo kuti: 14 “Kumapeto kwa zaka 7, aliyense wa inu azimasula mʼbale wake yemwe ndi Mheberi amene anagulitsidwa kwa inu ndipo wakutumikirani kwa zaka 6. Muzimulola kuti achoke.”+ Koma makolo anu sanandimvere ndipo sanatchere khutu lawo. 15 Ndipo inuyo posachedwapa* munasintha nʼkuchita zabwino pamaso panga polengeza ufulu kwa abale anu. Munachita pangano pamaso panga, mʼnyumba imene imatchulidwa ndi dzina langa. 16 Koma kenako munasinthanso nʼkuipitsa dzina langa+ potenganso akapolo anu aamuna ndi aakazi amene munawalola kuti achoke nʼkupita kulikonse kumene anafuna. Inu munawakakamiza kuti akhalenso akapolo anu.’
17 Choncho Yehova wanena kuti, ‘Inu simunamvere mawu anga oti mulengeze ufulu, aliyense kwa mʼbale wake ndi kwa mnzake.+ Tsopano ine ndikulengeza ufulu kwa inu,’ akutero Yehova. ‘Inu mudzafa ndi lupanga, mliri* ndi njala.+ Ndidzakusandutsani chinthu chimene maufumu onse apadziko lapansi adzachita nacho mantha.+ 18 Ndipo izi ndi zimene zidzachitikire anthu amene anaphwanya pangano langa posatsatira mawu a mʼpangano limene iwo anachita pamaso panga. Iwo anachita pangano limeneli podula mwana wa ngʼombe pakati nʼkudutsa pakati pa mbali ziwirizo.+ 19 Anthuwa ndi akalonga a Yuda, akalonga a Yerusalemu, nduna zapanyumba ya mfumu, ansembe ndi anthu onse amʼdzikoli amene anadutsa pakati pa mwana wa ngʼombe yemwe anamudula pakati. 20 Ndidzawapereka mʼmanja mwa adani awo ndi mʼmanja mwa onse amene akufuna moyo wawo. Mitembo yawo idzakhala chakudya cha mbalame zouluka mumlengalenga ndi zilombo zakutchire.+ 21 Ndipo Mfumu Zedekiya ya Yuda ndi akalonga ake ndidzawapereka mʼmanja mwa adani awo, mʼmanja mwa anthu amene akufuna moyo wawo ndiponso mʼmanja mwa asilikali a mfumu ya ku Babulo+ amene akubwerera osamenyana nanu.’+
22 Yehova wanena kuti, ‘Ndidzapereka lamulo ndipo ndidzachititsa kuti adaniwo abwererenso mumzinda uno. Iwo adzamenyana ndi mzindawu ndipo adzaulanda nʼkuuwotcha ndi moto.+ Mizinda ya Yuda ndidzaisandutsa bwinja ndipo simudzapezeka wokhalamo.’”+
35 Mʼmasiku a Yehoyakimu+ mwana wa Yosiya, mfumu ya Yuda, Yehova anauza Yeremiya kuti: 2 “Pita kunyumba ya Arekabu,+ ukalankhule nawo ndipo ukabwere nawo kunyumba ya Yehova. Ukalowe nawo mʼchimodzi mwa zipinda zodyera ndipo ukawapatse vinyo kuti amwe.”
3 Choncho ndinatenga Yaazaniya, mwana wa Yeremiya mwana wa Habaziniya, azibale ake, ana ake onse aamuna ndi banja lonse la Arekabu 4 nʼkuwabweretsa mʼnyumba ya Yehova. Ndinalowa nawo mʼchipinda chodyera cha ana a Hanani mwana wa Igadaliya, munthu wa Mulungu woona. Chipinda chimenechi chinali pafupi ndi chipinda chodyera cha akalonga chimene chinali pamwamba pa chipinda chodyera cha Maaseya mwana wa Salumu, amene anali mlonda wapakhomo. 5 Kenako ndinaika makapu ndi zipanda zodzaza ndi vinyo pamaso pa Arekabu nʼkuwauza kuti: “Imwani vinyoyu.”
6 Koma iwo anati: “Sitingamwe vinyo, chifukwa Yehonadabu*+ mwana wa Rekabu, kholo lathu, anatilamula kuti, ‘Inuyo kapena ana anu musamamwe vinyo mpaka kalekale. 7 Musamamange nyumba, musamafese mbewu komanso musamadzale kapena kukhala ndi minda ya mpesa. Koma nthawi zonse muzikhala mʼmatenti kuti mukhale ndi moyo wautali mʼdziko limene mukukhala ngati alendo.’ 8 Choncho ife tikupitiriza kumvera mawu a Yehonadabu mwana wa Rekabu kholo lathu, pa chilichonse chimene anatilamula. Timachita zimenezi popewa kumwa vinyo aliyense, ifeyo, akazi athu, ana athu aamuna ndi ana athu aakazi. 9 Sitimanga nyumba kuti tizikhalamo ndipo tilibe minda ya mpesa. Sitilima minda kapena kudzala mbewu. 10 Tikupitiriza kukhala mʼmatenti ndipo timamvera zonse zimene Yehonadabu* kholo lathu anatilamula. 11 Koma pamene Mfumu Nebukadinezara* ya Babulo inabwera kudzaukira dzikoli+ tinati, ‘Tiyeni tipite ku Yerusalemu kuti tithawe asilikali a Akasidi ndi asilikali a ku Siriya,’ ndipo pano tikukhala ku Yerusalemu.”
12 Yehova analankhula ndi Yeremiya kuti: 13 “Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti, ‘Pita ukauze anthu a ku Yuda komanso anthu amene akukhala mu Yerusalemu kuti: “Kodi inu simunkalimbikitsidwa nthawi zonse kuti muzimvera mawu anga?”+ akutero Yehova. 14 “Yehonadabu mwana wa Rekabu analamula ana ake kuti asamamwe vinyo ndipo iwo akhala akutsatira mawu ake moti samwa vinyo mpaka lero pomvera lamulo la kholo lawo.+ Koma ine ndakhala ndikulankhula nanu mobwerezabwereza,* koma simunandimvere.+ 15 Ndinkakutumizirani mobwerezabwereza*+ atumiki anga onse omwe anali aneneri. Ndinkawauza uthenga wakuti, ‘Chonde bwererani ndipo aliyense asiye njira zake zoipa.+ Muzichita zinthu zabwino. Musatsatire milungu ina nʼkumaitumikira. Mukatero mudzapitiriza kukhala mʼdziko limene ndinapatsa inuyo ndi makolo anu.’+ Koma inu simunatchere khutu kapena kundimvera. 16 Ana a Yehonadabu mwana wa Rekabu akhala akutsatira lamulo limene kholo lawo linawapatsa,+ koma anthu awa sanandimvere.”’”
17 “Choncho Yehova, Mulungu wa magulu ankhondo akumwamba, Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti, ‘Tsopano Yuda ndi anthu onse amene akukhala mu Yerusalemu ndiwagwetsera masoka onse amene ndinawachenjeza kuti ndidzawagwetsera.+ Ndichita zimenezi chifukwa ndakhala ndikulankhula nawo koma sanandimvere. Ndinkawaitana koma sanandiyankhe.’”+
18 Ndiyeno Yeremiya anauza anthu a mʼnyumba ya Rekabu kuti: “Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Chifukwa chakuti mwamvera lamulo la kholo lanu Yehonadabu ndipo mukupitiriza kusunga malamulo ake onse komanso kuchita zonse zimene anakulamulani, 19 Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Mulungu wa Isiraeli wanena kuti: “Sipadzalephera kukhala munthu wa mʼbanja la Yehonadabu* mwana wa Rekabu woti azitumikira pamaso panga nthawi zonse.”’”
36 Ndiyeno mʼchaka cha 4 cha ulamuliro wa Yehoyakimu+ mwana wa Yosiya, mfumu ya Yuda, Yehova anauza Yeremiya kuti: 2 “Tenga mpukutu ndipo ulembemo mawu onse amene ndakuuza okhudza chilango chimene ndidzapereke kwa Isiraeli, Yuda+ ndi mitundu yonse ya anthu.+ Ulembe mawu onse amene ndakuuza kuchokera nthawi imene ndinalankhula nawe mʼmasiku a Yosiya mpaka lero.+ 3 Mwina anthu a mʼnyumba ya Yuda akamva za masoka onse amene ndikufuna kuwagwetsera, adzabwerera nʼkusiya njira zawo zoipa. Akatero, ine ndidzawakhululukira zolakwa zawo ndi machimo awo.”+
4 Ndiyeno Yeremiya anaitana Baruki+ mwana wa Neriya nʼkumuuza mawu onse amene Yehova anamuuza ndipo Baruki analemba mawuwo mumpukutu.+ 5 Kenako Yeremiya anauza Baruki kuti: “Ine anditsekera ndipo sindingathe kukalowa mʼnyumba ya Yehova. 6 Choncho iweyo ndi amene ukuyenera kupita kukawerenga mokweza mawu a Yehova amene ali mumpukutu umene ndakuuza kuti ulembe. Ukawerenge mokweza pamaso pa anthu onse mʼnyumba ya Yehova pa tsiku losala kudya. Ukakatero ukakhala kuti wawerengera anthu onse a ku Yuda amene abwera kuchokera mʼmizinda yawo. 7 Mwina Yehova adzamva pempho lawo lakuti awakomere mtima ndipo aliyense adzabwerera nʼkusiya njira yake yoipa, popeza Yehova wanena kuti adzasonyeza anthu awa mkwiyo wake ndi ukali wake waukulu.”
8 Choncho Baruki mwana wa Neriya anachita zonse zimene mneneri Yeremiya anamulamula, kuti apite kunyumba ya Yehova kukawerenga mokweza mawu a Yehova amene analembedwa mumpukutumo.+
9 Ndiyeno mʼchaka cha 5 cha ulamuliro wa Yehoyakimu+ mwana wa Yosiya, mfumu ya Yuda, mʼmwezi wa 9, anthu onse a mu Yerusalemu ndi anthu onse amene anabwera ku Yerusalemu kuchokera mʼmizinda ya Yuda analengeza kuti asala kudya pamaso pa Yehova.+ 10 Kenako Baruki anawerenga mokweza mpukutu womwe unali ndi mawu a Yeremiya mʼnyumba ya Yehova. Anachita zimenezi mʼchipinda cha Gemariya+ mwana wa Safani+ wokopera Malemba,* mʼbwalo limene linali mʼmwamba, pakhomo la geti latsopano la nyumba ya Yehova,+ anthu onse akumva.
11 Mikaya mwana wa Gemariya, mwana wa Safani, atamva mawu onse a Yehova amene anali mumpukutumo, 12 anapita kunyumba ya mfumu, kuchipinda cha mlembi. Akalonga onse anali atakhala* pansi kumeneko ndipo kunali Elisama+ mlembi, Delaya mwana wa Semaya, Elinatani+ mwana wa Akibori,+ Gemariya mwana wa Safani, Zedekiya mwana wa Hananiya ndi akalonga ena onse. 13 Mikaya anawauza mawu onse amene anamva pamene Baruki ankawerenga mpukutuwo mokweza anthu onse akumva.
14 Zitatero, akalonga onse anatumiza Yehudi mwana wa Netaniya, mwana wa Selemiya, mwana wa Kusa, kukaitana Baruki kuti: “Bwera kuno ndipo utenge mpukutu umene unawerenga mokweza pamaso pa anthu onse.” Choncho Baruki mwana wa Neriya anatenga mpukutuwo nʼkupita nawo kwa iwo. 15 Akalongawo anamuuza kuti: “Khala pansi ndipo utiwerengere mokweza.” Choncho Baruki anawawerengera mpukutuwo.
16 Ndiyeno atamva mawu onsewa anayangʼanana mwamantha, ndipo anauza Baruki kuti: “Ndithu, tikuyenera kukauza mfumu mawu amenewa.” 17 Kenako anafunsa Baruki kuti: “Tiuze, zatheka bwanji kuti ulembe mawu onsewa. Kodi amachita kukuuza?” 18 Baruki anawayankha kuti: “Yeremiya amandiuza mawu onsewa, ine nʼkumalemba mumpukutuwu ndi inki.” 19 Akalongawo anauza Baruki kuti: “Iweyo ndi Yeremiya pitani mukabisale ndipo munthu aliyense asadziwe kumene muli.”+
20 Kenako akalongawo anapita kwa mfumu mʼbwalo la mkati nʼkusiya mpukutuwo mʼchipinda cha Elisama mlembi ndipo anauza mfumu zonse zimene anamva.
21 Mfumu itamva zimenezi inatuma Yehudi+ kuti akatenge mpukutuwo ndipo iye anakautenga mʼchipinda cha Elisama mlembi. Yehudi anayamba kuwerenga mokweza mpukutuwo pamaso pa mfumu ndi akalonga onse amene anaimirira pafupi ndi mfumuyo. 22 Pa nthawiyi nʼkuti mfumu ili mʼnyumba imene inkakhala mʼnyengo yozizira ndipo inkawotha moto wamʼmbaula. Umenewu unali mwezi wa 9.* 23 Yehudi akawerenga zigawo zitatu kapena 4 za mpukutuwo, mfumu inkadula mpukutuwo ndi mpeni wa mlembi nʼkuponya chidutswacho pamoto umene unali mʼmbaula uja. Inachita izi mpaka mpukutu wonsewo unathera pamotopo. 24 Iwo sanachite mantha ndipo mfumu ndi atumiki ake onse amene ankamvetsera mawuwa sanangʼambe zovala zawo. 25 Ngakhale kuti Elinatani,+ Delaya+ ndi Gemariya+ anachonderera mfumu kuti isawotche mpukutuwo, mfumuyo sinawamvere. 26 Komanso mfumu inalamula Yerameeli mwana wa mfumu, Seraya mwana wa Azirieli ndi Selemiya mwana wa Abideeli kuti akagwire Baruki mlembi ndi mneneri Yeremiya, koma Yehova anawabisa.+
27 Mfumu itawotcha mpukutu umene unali ndi mawu amene Baruki analemba atauzidwa ndi Yeremiya, Yehova analankhulanso ndi Yeremiya+ kuti: 28 “Tenga mpukutu wina ndipo ulembemo mawu onse amene anali mumpukutu woyamba uja, umene Yehoyakimu mfumu ya Yuda wawotcha.+ 29 Ponena za Yehoyakimu mfumu ya Yuda unene kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Iwe wawotcha mpukutuwu nʼkunena kuti, ‘Nʼchifukwa chiyani walemba mumpukutuwu kuti: “Mfumu ya Babulo idzabwera ndithu kudzawononga dziko lino ndipo simudzapezeka nyama ndi munthu wokhalamo”?’+ 30 Choncho ponena za chilango chimene adzapatse Yehoyakimu mfumu ya Yuda, Yehova wanena kuti, ‘Sipadzapezeka mwana wake aliyense wokhala pampando wachifumu wa Davide+ ndipo mtembo wake udzakhala padzuwa lotentha masana ndipo usiku udzakhala panja pozizira.+ 31 Ine ndidzaimba mlandu Yehoyakimu, ana ake* ndi atumiki ake chifukwa cha zolakwa zawo. Anthu amenewa komanso anthu amene akukhala mu Yerusalemu ndi mu Yuda ndidzawagwetsera masoka onse amene ndanena+ chifukwa sanamvere.’”’”+
32 Kenako Yeremiya anatenga mpukutu wina nʼkupatsa Baruki mlembi,+ mwana wa Neriya. Baruki analembamo mawu onse amene Yeremiya anamuuza, amene anali mumpukutu umene Yehoyakimu mfumu ya Yuda inawotcha.+ Mumpukutumo anawonjezeramo mawu ena ambiri ochokera kwa Mulungu.
37 Ndiyeno Mfumu Zedekiya+ mwana wa Yosiya inayamba kulamulira mʼmalo mwa Koniya+ mwana wa Yehoyakimu chifukwa Mfumu Nebukadinezara* ya Babulo inamuika kuti akhale mfumu mʼdziko la Yuda.+ 2 Koma Zedekiyayo, atumiki ake ndi anthu amʼdzikolo sanamvere mawu amene Yehova ananena kudzera mwa mneneri Yeremiya.
3 Ndiyeno Mfumu Zedekiya inatuma Yehukali+ mwana wa Selemiya ndi Zefaniya+ mwana wa Maaseya wansembe kwa mneneri Yeremiya kukamuuza kuti: “Chonde, tipempherere kwa Yehova Mulungu wathu.” 4 Yeremiya ankakhala mwaufulu pakati pa anthuwo chifukwa anali asanamutsekere mʼndende.+ 5 Ndiyeno asilikali a Farao anabwera kuchokera ku Iguputo+ ndipo Akasidi amene anali atazungulira mzinda wa Yerusalemu atamva zimenezi anachoka ku Yerusalemu.+ 6 Kenako Yehova anauza mneneri Yeremiya kuti: 7 “Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Mfumu ya Yuda imene yakutumani kudzafunsira kwa ine mukaiuze kuti: “Taonani! Asilikali a Farao amene akubwera kudzakuthandizani adzabwerera kwawo ku Iguputo.+ 8 Ndipo Akasidi adzabweranso kudzamenyana ndi mzinda uno, adzaulanda nʼkuuwotcha ndi moto.”+ 9 Yehova wanena kuti: “Musadzipusitse ponena kuti, ‘Akasidi samenyana nafe, ndithu abwerera,’ chifukwa sachoka ayi. 10 Ngakhale mutapha pafupifupi asilikali onse a Akasidi amene akumenyana nanu nʼkungotsala ovulala kwambiri okha, iwo angadzukebe mʼmatenti awo nʼkuwotcha mzindawu ndi moto.”’”+
11 Asilikali a Akasidi atabwerera kuchoka ku Yerusalemu chifukwa cha asilikali a Farao,+ 12 Yeremiya ananyamuka kuchoka ku Yerusalemu kupita kudziko la Benjamini+ kuti akalandire cholowa chake pakati pa anthu ake. 13 Koma mneneri Yeremiya atafika pa Geti la Benjamini, mkulu wa alonda amene dzina lake linali Iriya mwana wa Selemiya, mwana wa Hananiya, anamugwira nʼkunena kuti: “Ukuthawira kwa Akasidi iwe!” 14 Yeremiya anamuyankha kuti: “Zabodza zimenezo! Ine sindikuthawira kwa Akasidi.” Koma Iriya sanamumvere. Choncho Iriya anagwira Yeremiya nʼkumupititsa kwa akalonga. 15 Akalongawo anakwiyira kwambiri Yeremiya+ ndipo anamumenya nʼkumutsekera*+ mʼnyumba ya Yehonatani mlembi, imene anaisandutsa ndende. 16 Yeremiya anamuika mʼndende yapansi,* muselo ndipo anakhala mmenemo kwa masiku ambiri.
17 Kenako Mfumu Zedekiya inatuma anthu kuti akatenge Yeremiya.+ Atabwera naye, mfumuyo inamufunsa mafunso mwachinsinsi mʼnyumba mwake. Mfumuyo inamufunsa kuti: “Kodi pali mawu aliwonse ochokera kwa Yehova?” Yeremiya anayankha kuti: “Eya alipo!” Ndipo anapitiriza kuti: “Inuyo mudzaperekedwa mʼmanja mwa mfumu ya Babulo!”+
18 Yeremiya anafunsanso Mfumu Zedekiya kuti: “Kodi ineyo ndakulakwirani chiyani pamodzi ndi atumiki anu ndiponso anthuwa, kuti munditsekere mʼndende? 19 Tsopano ali kuti aneneri anu amene ankalosera kwa inu kuti, ‘Mfumu ya Babulo sidzabwera kudzamenyana ndi inu ndiponso dzikoliʼ?+ 20 Ndiye ndimvereni chonde, mbuyanga mfumu. Chonde, imvani pempho langa lakuti mundikomere mtima. Musandibwezere kunyumba ya Yehonatani+ mlembi, chifukwa ndingakafere kumeneko.”+ 21 Choncho Mfumu Zedekiya inalamula kuti Yeremiya atsekeredwe mʼBwalo la Alonda+ ndipo tsiku lililonse ankamupatsa mtanda wozungulira wa mkate.+ Mkate umenewu unkachokera kumsewu wa ophika mkate ndipo anapitiriza kumʼpatsa mkatewo mpaka mkate wonse utatha mumzindamo.+ Choncho Yeremiya anapitiriza kukhala mʼBwalo la Alonda.
38 Ndiyeno Sefatiya mwana wa Mateni, Gedaliya mwana wa Pasuri,+ Yukali+ mwana wa Selemiya ndi Pasuri mwana wa Malikiya anamva mawu onse amene Yeremiya ankauza anthu onse kuti: 2 “Yehova wanena kuti, ‘Amene atsale mumzinda uno adzafa ndi lupanga, njala ndi mliri.*+ Koma amene adzadzipereke* kwa Akasidi adzapitiriza kukhala ndi moyo. Adzapulumutsa moyo wake, sadzafa ayi.’+ 3 Yehova wanena kuti, ‘Mzinda uno udzaperekedwa ndithu mʼmanja mwa asilikali a mfumu ya Babulo ndipo mfumuyo idzaulanda.’”+
4 Akalonga anauza mfumu kuti: “Chonde lamulani kuti munthu uyu aphedwe+ chifukwa akufooketsa asilikali amene atsala mumzinda uno komanso anthu onse, powauza mawu amenewa. Munthu ameneyu sakuwafunira mtendere anthuwa, koma akuwafunira tsoka.” 5 Mfumu Zedekiya inawayankha kuti: “Taonani! Iye ali mʼmanja mwanu, ndipo palibe chilichonse chimene ndingachite kuti ndikuletseni.”
6 Choncho iwo anagwira Yeremiya nʼkumuponya mʼchitsime cha Malikiya mwana wa mfumu, chimene chinali mʼBwalo la Alonda.+ Iwo analowetsa Yeremiya mʼchitsimemo pogwiritsa ntchito zingwe. Mʼchitsimemo munalibe madzi koma munali matope ndipo Yeremiya anayamba kumira mʼmatopemo.
7 Ebedi-meleki+ wa ku Itiyopiya, amene anali nduna mʼnyumba ya mfumu, anamva kuti Yeremiya amuponya mʼchitsime. Apa nʼkuti mfumu itakhala pa Geti la Benjamini.+ 8 Choncho Ebedi-meleki anatuluka mʼnyumba ya mfumuyo ndipo anakauza mfumu kuti: 9 “Inu mbuyanga mfumu, zimene anthu awa achitira mneneri Yeremiya ndi zoipa. Iwo amuponya mʼchitsime ndipo afera momwemo chifukwa cha njala, popeza mkate watheratu mumzindawu.”+
10 Kenako mfumu inalamula Ebedi-meleki wa ku Itiyopiya kuti: “Tenga amuna 30 kunoko, ndipo mukatulutse mneneri Yeremiya mʼchitsimemo asanafe.” 11 Choncho Ebedi-meleki anatenga amunawo ndipo analowa mʼnyumba ya mfumu, mʼchipinda chimene chinali pansi pa malo osungira chuma.+ Kumeneko anatengako nsanza ndi nsalu zakutha nʼkuzilowetsa mʼchitsime momwe munali Yeremiya pogwiritsa ntchito zingwe. 12 Ndiyeno Ebedi-meleki wa ku Itiyopiya anauza Yeremiya kuti: “Nsanza komanso nsalu zakuthazo uzikulunge kuzingwezo nʼkuziika mʼkhwapa.” Yeremiya anachitadi zimenezo, 13 ndipo iwo anakoka Yeremiya ndi zingwezo nʼkumutulutsa mʼchitsimemo. Yeremiya anapitiriza kukhala mʼBwalo la Alonda.+
14 Mfumu Zedekiya inatumiza anthu kuti akaitane mneneri Yeremiya kuti abwere kwa iye pakhomo lachitatu lamʼnyumba ya Yehova. Yeremiya atafika, mfumu inamuuza kuti: “Ndikufuna ndikufunse zinazake. Usandibisire kalikonse.” 15 Yeremiya anauza Zedekiya kuti: “Ndikakuuzani, ndithu mundipha. Komanso ndikakupatsani malangizo, simundimvera.” 16 Choncho Mfumu Zedekiya inalumbira kwa Yeremiya mwachinsinsi kuti: “Pali Yehova Mulungu wamoyo, amene anatipatsa moyowu, sindikupha ndiponso sindikupereka mʼmanja mwa anthu awa amene akufuna kuchotsa moyo wako.”
17 Ndiyeno Yeremiya anauza Zedekiya kuti: “Yehova, Mulungu wa magulu ankhondo akumwamba, Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Mukadzipereka mʼmanja mwa akalonga* a mfumu ya Babulo, mudzakhalabe ndi moyo ndipo mzindawu sudzawotchedwa ndi moto komanso inuyo ndi banja lanu mudzakhalabe ndi moyo.+ 18 Koma ngati simudzadzipereka mʼmanja mwa akalonga* a mfumu ya Babulo, mzindawu udzaperekedwa mʼmanja mwa Akasidi ndipo adzauwotcha ndi moto.+ Inuyo simudzathawa mʼmanja mwawo.’”+
19 Ndiyeno Mfumu Zedekiya inauza Yeremiya kuti: “Ndikuopa Ayuda amene athawira kwa Akasidi chifukwa ngati ndingaperekedwe mʼmanja mwawo akhoza kundizunza.” 20 Koma Yeremiya anauza mfumuyo kuti: “Sadzakuperekani mʼmanja mwawo. Chonde, mverani mawu a Yehova amene ndikukuuzani. Mukatero zinthu zidzakuyenderani bwino ndipo mudzakhalabe ndi moyo. 21 Koma mukakana kudzipereka mʼmanja mwawo,* Yehova wandiululira izi: 22 Taonani! Akazi onse amene anatsala mʼnyumba ya mfumu ya Yuda akupita nawo kwa akalonga a mfumu ya Babulo,+ ndipo akaziwo akunena kuti,
‘Amuna amene munkawadalira* akuputsitsani ndipo akugonjetsani.+
Achititsa kuti mapazi anu amire mʼmatope
Tsopano akubwerera ndipo akusiyani.’
23 Akazi anu onse ndi ana anu aamuna akupita nawo kwa Akasidi ndipo inuyo simudzathawa mʼmanja mwawo. Koma mfumu ya Babulo+ idzakugwirani ndipo mzindawu udzawotchedwa chifukwa cha inu.”+
24 Kenako Zedekiya anauza Yeremiya kuti: “Munthu aliyense asadziwe zimenezi, kuti usafe. 25 Ngati akalonga atamva kuti ndalankhula nawe, nʼkubwera kwa iwe kudzakuuza kuti, ‘Chonde tiuze zimene unalankhula ndi mfumu, usatibisire kalikonse ndipo sitikupha.+ Kodi mfumu yakuuza chiyani?’ 26 Uwauze kuti, ‘Ndimapempha mfumu kuti isandibwezere kunyumba ya Yehonatani chifukwa ndingakafere kumeneko.’”+
27 Patapita nthawi, akalonga onse anafika kwa Yeremiya nʼkumufunsa mafunso. Yeremiya anawayankha mogwirizana ndi zonse zimene mfumu inamulamula kuti anene. Choncho akalongawo sananenenso chilichonse chifukwa sanamve zimene anakambirana. 28 Yeremiya anapitirizabe kukhala mʼBwalo la Alonda+ mpaka tsiku limene Yerusalemu analandidwa. Iye anali adakali konko pamene Yerusalemu analandidwa.+
39 Mʼchaka cha 9 cha ulamuliro wa Mfumu Zedekiya ya Yuda, mʼmwezi wa 10, Mfumu Nebukadinezara* ya Babulo ndi asilikali ake onse anafika ku Yerusalemu nʼkuzungulira mzindawo.+
2 Mʼchaka cha 11 cha ulamuliro wa Zedekiya, mʼmwezi wa 4, pa tsiku la 9, anaboola mpanda wa mzindawo.+ 3 Ndiyeno akalonga onse a mfumu ya Babulo analowa mumzindawo nʼkukhala pansi pa Geti la Pakati.+ Mayina awo anali Nerigali-sarezera amene anali Samugari, Nebo-sarisekimu amene anali Rabisarisi,* Nerigali-sarezera amene anali Rabimagi* ndi akalonga ena onse a mfumu ya Babulo.
4 Mfumu Zedekiya ya Yuda ndi asilikali onse ataona adaniwo, anathawira+ kunja kwa mzinda usiku. Iwo anadzera njira yakumunda wa mfumu nʼkukadutsa pageti limene linali pakati pa makoma awiri ndipo anapitiriza kuthawa kulowera ku Araba.+ 5 Koma asilikali a Akasidi anawathamangitsa ndipo Zedekiya anamupeza mʼchipululu cha Yeriko.+ Anamugwira nʼkupita naye kwa Mfumu Nebukadinezara* ya Babulo ku Ribila,+ mʼdziko la Hamati,+ kumene Nebukadinezara anamuweruza. 6 Zitatero mfumu ya Babulo inapha ana aamuna a Zedekiya ku Ribila, Zedekiyayo akuona. Inaphanso anthu onse olemekezeka a ku Yuda.+ 7 Mfumu ya Babulo inachititsa khungu maso a Zedekiya ndipo kenako inamumanga mʼmaunyolo akopa* kuti apite naye ku Babulo.+
8 Kenako Akasidi anawotcha nyumba ya mfumu ndi nyumba za anthu+ ndipo anagwetsa mpanda wa Yerusalemu.+ 9 Nebuzaradani+ mkulu wa asilikali olondera mfumu, anatenga anthu ena onse otsala mumzindamo, anthu amene anathawira kwa mfumu ya Babulo ndi anthu ena onse amene anapulumuka nʼkupita nawo ku ukapolo ku Babulo.
10 Koma Nebuzaradani mkulu wa asilikali olondera mfumu, anasiya mʼdziko la Yuda ena mwa anthu amene anali osauka kwambiri omwe analibe kalikonse. Pa tsiku limenelo anawapatsanso minda ndi minda ya mpesa kuti azilima.*+
11 Mfumu Nebukadinezara* ya Babulo inapereka lamulo kwa Nebuzaradani mkulu wa asilikali olondera mfumu lokhudza Yeremiya kuti: 12 “Mutenge uzimuyangʼanira ndipo usamuchitire choipa chilichonse. Koma uzimupatsa chilichonse chimene iye wapempha.”+
13 Choncho Nebuzaradani mkulu wa asilikali olondera mfumu ndi Nebusazibani amene anali Rabisarisi,* Nerigali-sarezera amene anali Rabimagi* ndi akuluakulu onse a mfumu ya Babulo anatuma anthu. 14 Iwo anatuma anthuwo kuti akatenge Yeremiya mʼBwalo la Alonda+ nʼkumupereka kwa Gedaliya+ mwana wa Ahikamu,+ mwana wa Safani,+ kuti apite naye kunyumba kwake. Choncho Yeremiya anayamba kukhala ndi anthu.
15 Pa nthawi imene Yeremiya anatsekeredwa mʼBwalo la Alonda,+ Yehova analankhula naye kuti: 16 “Pita kwa Ebedi-meleki+ wa ku Itiyopiya ndipo ukamuuze kuti, ‘Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti: “Taona! Ndikukwaniritsa mawu anga akuti mzinda uwu ndidzaugwetsera tsoka osati zinthu zabwino ndipo pa tsikulo iweyo udzaona zimenezi zikuchitika.”’
17 ‘Koma pa tsikulo iweyo ndidzakupulumutsa ndipo sudzaperekedwa mʼmanja mwa anthu amene ukuwaopa,’ akutero Yehova.
18 ‘Chifukwa ine ndidzakupulumutsa ndithu ndipo sudzaphedwa ndi lupanga. Udzapulumuka+ chifukwa chakuti wandikhulupirira,’+ akutero Yehova.”
40 Awa ndi mawu amene Yehova anauza Yeremiya pambuyo poti Nebuzaradani+ mkulu wa asilikali olondera mfumu wamumasula kuchoka ku Rama.+ Nebuzaradani anatenga Yeremiya kumeneko atamangidwa maunyolo amʼmanja ndipo anali mʼgulu la anthu onse a ku Yerusalemu ndi a ku Yuda amene anatengedwa kupita ku ukapolo ku Babulo. 2 Ndiyeno mkulu wa asilikali olondera mfumuyu anatengera Yeremiya pambali nʼkumuuza kuti: “Yehova Mulungu wako ananeneratu kuti tsoka ili lidzagwera dziko lino 3 ndipo Yehova wabweretsadi tsokali mogwirizana ndi zimene ananenazo, chifukwa anthu inu munachimwira Yehova ndipo simunamvere mawu ake. Nʼchifukwa chake zimenezi zakuchitikirani.+ 4 Lero ndikumasula maunyolo amene ali mʼmanja mwako. Ngati ungakonde kupita nane ku Babulo, tiye ndipo ndizikakuyangʼanira. Koma ngati sukufuna kupita nane ku Babulo, usapite. Taona! Dziko lonse lili pamaso pako. Pita kulikonse kumene ungakonde.”+
5 Yeremiya akuganizira koti apite, Nebuzaradani anamuuza kuti: “Bwerera kwa Gedaliya,+ mwana wa Ahikamu,+ mwana wa Safani,+ amene mfumu ya Babulo yamuika kuti azilamulira mizinda ya Yuda. Ukakhale naye pakati pa anthuwo, kapena ukhoza kupita kulikonse kumene ungakonde.”
Kenako mkulu wa asilikali olondera mfumu anamupatsa chakudya chapaulendo ndi mphatso ndipo anamulola kuti apite. 6 Choncho Yeremiya anapita ku Mizipa+ kwa Gedaliya, mwana wa Ahikamu nʼkumakhala naye limodzi ndi anthu amene anatsala mʼdziko la Yuda.
7 Patapita nthawi, akuluakulu onse a asilikali amene anali mʼdziko lonselo limodzi ndi asilikali awo, anamva kuti mfumu ya Babulo yaika Gedaliya mwana wa Ahikamu kuti akhale wolamulira dzikolo. Anamvanso kuti yamuika kuti azilamulira amuna, akazi ndi ana ochokera pakati pa anthu osauka mʼdzikolo amene sanatengedwe kupita ku Babulo.+ 8 Choncho akuluakulu amenewa anapita kwa Gedaliya ku Mizipa.+ Mayina awo anali Isimaeli+ mwana wa Netaniya, Yohanani+ ndi Yonatani ana a Kareya, Seraya mwana wa Tanumeti, ana a Efai wa ku Netofa, Yezaniya+ mwana wa munthu wa ku Maaka limodzi ndi asilikali awo. 9 Gedaliya mwana wa Ahikamu mwana wa Safani analumbira pamaso pa akuluakuluwo ndi asilikali awo kuti: “Musaope kutumikira Akasidi. Zikhalani mʼdzikoli nʼkumatumikira mfumu ya Babulo ndipo zinthu zidzakuyenderani bwino.+ 10 Koma ine ndizikhala ku Mizipa kuno kuti ndizikuimirirani kwa* Akasidi amene azibwera kwa ife. Koma inuyo musonkhanitse vinyo, zipatso zamʼchilimwe* ndi mafuta nʼkuziika mʼziwiya zanu zosungira zinthu ndipo muzikhala mʼmizinda imene mwaitenga kuti ikhale yanu.”+
11 Ndiye Ayuda onse amene anali ku Mowabu, ku Amoni, ku Edomu komanso amene anali mʼmayiko ena onse anamvanso kuti mfumu ya Babulo yalola kuti anthu amene anatsala azikhala ku Yuda komanso kuti yaika Gedaliya mwana wa Ahikamu mwana wa Safani kuti aziwalamulira. 12 Choncho Ayuda onse anayamba kubwerera kuchokera kumadera onse kumene anawabalalitsira ndipo anabwera mʼdziko la Yuda kwa Gedaliya ku Mizipa. Iwo anasonkhanitsa vinyo ndi zipatso zamʼchilimwe zochuluka kwambiri.
13 Nayenso Yohanani mwana wa Kareya ndi akuluakulu onse a asilikali amene anali mʼdziko lonselo, anabwera kwa Gedaliya ku Mizipa. 14 Iwo anauza Gedaliya kuti: “Kodi sukudziwa kuti Baalisi mfumu ya a Amoni,+ watumiza Isimaeli mwana wa Netaniya kuti adzakuphe?”+ Koma Gedaliya mwana wa Ahikamu sanawakhulupirire.
15 Kenako Yohanani mwana wa Kareya anauza mwachinsinsi Gedaliya ku Mizipa kuti: “Ndikufuna ndipite kukapha Isimaeli mwana wa Netaniya ndipo palibe amene adziwe. Nʼchifukwa chiyani iyeyo akufuna kukupha? Nʼchifukwa chiyani akufuna kuti anthu onse a mu Yuda amene akubwera kwa iwe amwazike komanso kuti anthu amene anatsala mu Yuda awonongeke?” 16 Koma Gedaliya+ mwana wa Ahikamu anauza Yohanani mwana wa Kareya kuti: “Usachite zimenezi chifukwa zimene ukunena zokhudza Isimaeli, ndi zabodza.”
41 Mʼmwezi wa 7, Isimaeli+ mwana wa Netaniya, mwana wa Elisama, anapita kwa Gedaliya mwana wa Ahikamu ku Mizipa+ pamodzi ndi amuna ena 10. Isimaeli anali wa mʼbanja lachifumu* ndipo analinso mmodzi mwa akuluakulu a mfumu. Pamene ankadyera limodzi chakudya ku Mizipa, 2 Isimaeli mwana wa Netaniya ndi amuna 10 amene anali naye ananyamuka nʼkupha ndi lupanga Gedaliya mwana wa Ahikamu, mwana wa Safani. Choncho Isimaeli anapha munthu amene mfumu ya Babulo inamuika kuti azilamulira dzikolo. 3 Isimaeli anaphanso Ayuda onse amene anali ndi Gedaliya ku Mizipa komanso asilikali a Akasidi amene anali kumeneko.
4 Pa tsiku lachiwiri kuchokera pamene Gedaliya anaphedwa, munthu aliyense asanadziwe zimenezi, 5 kunabwera amuna 80 ochokera ku Sekemu,+ ku Silo+ ndi ku Samariya.+ Iwo anabwera atameta ndevu, atangʼamba zovala zawo ndiponso atadzichekacheka.+ Amunawa anabwera atanyamula nsembe yambewu komanso lubani+ kuti adzazipereke kunyumba ya Yehova. 6 Ndiyeno Isimaeli mwana wa Netaniya ananyamuka ku Mizipa akulira kuti akakumane nawo. Atakumana nawo anawauza kuti: “Tiyeni kwa Gedaliya mwana wa Ahikamu.” 7 Koma anthuwo atafika mumzinda, Isimaeli mwana wa Netaniya ndi amuna amene anali naye anawapha nʼkuwaponya mʼchitsime.
8 Koma pakati pa anthuwo panali amuna 10 amene anauza Isimaeli kuti: “Usatiphe chifukwa tili ndi nkhokwe za tirigu, barele, mafuta ndi uchi zimene tinazibisa mʼmunda.” Choncho Isimaeli anawasiya ndipo sanawaphe ngati mmene anachitira ndi abale awo. 9 Isimaeli anaponya mitembo yonse ya amuna amene anawapha mʼchitsime chachikulu kwambiri. Mfumu Asa ndi imene inakumba chitsime chimenechi pamene Basa mfumu ya Isiraeli+ inamuopseza. Chitsime chimenechi ndi chimene Isimaeli mwana wa Netaniya anaponyamo mitembo ya anthu amene anawapha.
10 Isimaeli anagwira anthu ena onse amene anali ku Mizipa,+ kuphatikizapo ana aakazi a mfumu ndi anthu ena onse amene anatsala ku Mizipa omwe Nebuzaradani mkulu wa asilikali olondera mfumu anawapereka kwa Gedaliya+ mwana wa Ahikamu kuti aziwayangʼanira. Isimaeli mwana wa Netaniya anawagwira ndipo ananyamuka kuti awolokere nawo kudziko la Aamoni.+
11 Yohanani+ mwana wa Kareya ndi akuluakulu onse a asilikali amene anali naye atamva zoipa zonse zimene Isimaeli mwana wa Netaniya anachita, 12 anatenga asilikali onse nʼkupita kukamenyana ndi Isimaeli mwana wa Netaniya ndipo anamupeza pafupi ndi madzi ambiri a ku Gibiyoni.*
13 Anthu onse amene anali ndi Isimaeli anasangalala kwambiri ataona Yohanani mwana wa Kareya ndi akuluakulu onse a asilikali amene anali naye. 14 Ndiyeno anthu onse amene Isimaeli anawagwira ku Mizipa+ anathawa nʼkubwerera limodzi ndi Yohanani mwana wa Kareya. 15 Koma Isimaeli mwana wa Netaniya limodzi ndi amuna 8, anathawa ataona Yohanani ndipo anapita kwa Aamoni.
16 Ndiyeno Yohanani mwana wa Kareya ndi akuluakulu onse a asilikali amene anali naye anatenga anthu onse amene anatsala ku Mizipa. Anthu amenewa ndi amene anawapulumutsa mʼmanja mwa Isimaeli mwana wa Netaniya amene anawagwira atapha Gedaliya+ mwana wa Ahikamu. Anapulumutsa amuna, asilikali, akazi, ana ndi nduna zapanyumba ya mfumu ndipo anabwera nawo kuchokera ku Gibiyoni. 17 Iwo anakakhala kumalo ogona alendo a Chimamu pafupi ndi Betelehemu+ nʼcholinga choti apitirize ulendo wopita ku Iguputo.+ 18 Anachita zimenezi chifukwa cha Akasidi. Iwo ankaopa Akasidiwo chifukwa chakuti Isimaeli mwana wa Netaniya anapha Gedaliya mwana wa Ahikamu, amene mfumu ya Babulo inamuika kuti azilamulira mʼdzikolo.+
42 Kenako akuluakulu onse a asilikali, Yohanani+ mwana wa Kareya, Yezaniya mwana wa Hoshaya ndi anthu onse kuyambira anthu wamba mpaka anthu olemekezeka, anapita 2 kwa mneneri Yeremiya nʼkumuuza kuti: “Chonde, tikomere mtima ndipo utipempherere kwa Yehova Mulungu wako. Pempherera anthu onse amene atsalawa chifukwa poyamba tinalipo ambiri koma pano tatsala ochepa+ ngati mmene ukuoneramu. 3 Yehova Mulungu wako atiuze njira yoti tiyendemo ndi zoti tichite.”
4 Mneneri Yeremiya anawayankha kuti: “Ndamva zimene mwanenazo. Ndipemphera kwa Yehova Mulungu wanu malinga ndi zimene mwapempha. Ndipo mawu aliwonse amene Yehova angakuyankheni ndidzakuuzani. Sindidzakubisirani chilichonse.”
5 Iwo anayankha Yeremiya kuti: “Yehova akhale mboni yoona ndi yokhulupirika, ndipo atilange ngati sitidzachita ndendende mogwirizana ndi malangizo amene Yehova Mulungu wako angatipatse kudzera mwa iwe. 6 Ife tikukutuma kwa Yehova Mulungu wathu, kaya mawu ake ndi otikomera kapena otiipira, tidzamverabe mawuwo. Tidzachita zimenezi kuti zinthu zitiyendere bwino chifukwa chomvera mawu a Yehova Mulungu wathu.”
7 Ndiye patadutsa masiku 10, Yehova analankhula ndi Yeremiya. 8 Choncho Yeremiya anaitana Yohanani mwana wa Kareya, pamodzi ndi akuluakulu onse a asilikali amene anali naye. Anaitananso anthu onse, anthu wamba ndi anthu olemekezeka omwe.+ 9 Iye anawauza kuti: “Inu munandituma kwa Yehova Mulungu wa Isiraeli kukamupempha kuti akukomereni mtima. Ndiye zimene iye wanena ndi izi: 10 ‘Ngati mungakhalebe mʼdziko lino, ndidzakumangani osati kukugwetsani, ndidzakudzalani osati kukuzulani, popeza ndidzakumverani chisoni chifukwa cha tsoka limene ndakugwetserani.+ 11 Musachite mantha ndi mfumu ya Babulo imene mukuiopayo.’+
‘Mfumu imeneyi musachite nayo mantha, chifukwa ine ndili ndi inu kuti ndikupulumutseni ndi kukulanditsani mʼmanja mwake,’ akutero Yehova. 12 ‘Ndidzakuchitirani chifundo+ moti mfumuyo idzakumverani chifundo nʼkukubwezerani kudziko lanu.
13 Koma inu mukanena kuti: “Ayi! Ife sitikhala mʼdziko lino,” ndipo mukapanda kumvera mawu a Yehova Mulungu wanu 14 ponena kuti, “Ayi, mʼmalomwake tipita kudziko la Iguputo,+ kumene sitidzaona nkhondo kapena kumva kulira kwa lipenga komanso kumene sitidzasowa chakudya. Ife tizikakhala kumeneko,” 15 imvani mawu a Yehova, inu otsala a Yuda. Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Mulungu wa Isiraeli wanena kuti: “Ngati mwatsimikiza mtima kuti mupite ku Iguputo ndipo mukapitadi nʼkukakhala* kumeneko, 16 ndiye kuti lupanga limene mukuliopa lidzakupezani ku Iguputo komweko ndipo njala imene mukuiopa idzakutsatirani ku Iguputoko moti mudzafera komweko.+ 17 Ndipo amuna onse amene atsimikiza mtima kupita ku Iguputo kuti akakhale kumeneko adzafa ndi lupanga, njala ndi mliri.* Palibe amene adzapulumuke kapena kuthawa tsoka limene ndidzawagwetsere.”’
18 Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti: ‘Mofanana ndi mmene ndinasonyezera anthu okhala mu Yerusalemu+ mkwiyo ndi ukali wanga, inunso ndidzakusonyezani mkwiyo wanga ngati mutapita ku Iguputo. Mudzakhala otembereredwa, chinthu chochititsa mantha, chinthu chonyozeka+ ndi chochititsa manyazi ndipo malo ano simudzawaonanso.’
19 Yehova wakuuzani inu otsala a Yuda, kuti musapite ku Iguputo. Dziwani ndithu kuti ine ndakuchenjezani lero 20 kuti zolakwa zanu zidzakuphetsani. Zili choncho chifukwa inu munandituma kwa Yehova Mulungu wanu kuti, ‘Tipempherere kwa Yehova Mulungu wathu ndipo udzatiuze zilizonse zimene Yehova Mulungu wathu adzanene ndipo ife tidzachita zomwezo.’+ 21 Ndipo ine ndakuuzani lero, koma inu simumvera mawu a Yehova Mulungu wanu kapena kuchita chilichonse chimene wandituma kuti ndidzakuuzeni.+ 22 Choncho dziwani ndithu kuti mudzafa ndi lupanga, njala ndi mliri mʼdziko limene mukulakalaka kupita kuti muzikakhalako.”+
43 Yeremiya atamaliza kuuza anthu onse mawu onsewa ochokera kwa Yehova Mulungu wawo, mawu onse amene Yehova Mulungu wawo anamutuma kuti akawauze, 2 Azariya mwana wa Hoshaya, Yohanani+ mwana wa Kareya ndi anthu onse odzikuza anauza Yeremiya kuti: “Zimene ukunenazo ndi zabodza! Yehova Mulungu wathu sanakutume kuti udzatiuze kuti, ‘Musapite ku Iguputo kuti mukakhale kumeneko.’ 3 Koma Baruki+ mwana wa Neriya ndi amene akukulimbikitsa kuti unene zinthu zofuna kutipweteketsa nʼcholinga choti mutipereke mʼmanja mwa Akasidi kuti atiphe kapena atitenge kupita ku ukapolo ku Babulo.”+
4 Choncho Yohanani mwana wa Kareya, akuluakulu onse a asilikali ndi anthu onse sanamvere mawu a Yehova oti apitirize kukhala mʼdziko la Yuda. 5 Mʼmalomwake, Yohanani mwana wa Kareya ndi akuluakulu onse a asilikali anatenga anthu onse amene anatsala ku Yuda amene anabwerera kuchokera ku mitundu yonse ya anthu kumene anathawira kuti adzakhale mʼdziko la Yuda.+ 6 Anatenga amuna, akazi, ana, ana aakazi a mfumu ndiponso aliyense amene Nebuzaradani+ mkulu wa asilikali olondera mfumu anawasiya mʼmanja mwa Gedaliya+ mwana wa Ahikamu,+ mwana wa Safani.+ Anatenganso mneneri Yeremiya ndi Baruki mwana wa Neriya. 7 Iwo anapita mʼdziko la Iguputo chifukwa sanamvere mawu a Yehova ndipo anakafika ku Tahapanesi.+
8 Ndiyeno pamene Yeremiya anali ku Tahapanesi, Yehova anamuuza kuti: 9 “Tenga miyala ikuluikulu ndipo ukaibise mʼdothi limene anamangira masitepe a njerwa amene ali pakhomo la nyumba ya Farao ku Tahapanesi. Ukachite zimenezi amuna onse a Chiyuda akuona. 10 Kenako ukawauze kuti, ‘Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Mulungu wa Isiraeli wanena kuti: “Ine ndikuitana Nebukadinezara* mfumu ya Babulo mtumiki wanga,+ ndipo ndidzaika mpando wake wachifumu pamwamba penipeni pa miyala imene ndaibisayi. Iye adzamanga tenti yake yachifumu pamwamba pa miyala imeneyi.+ 11 Nebukadinezara adzabwera nʼkuukira dziko la Iguputo.+ Woyenera kufa ndi mliri adzafa ndi mliri. Woyenera kutengedwa kupita ku ukapolo adzatengedwa kupita ku ukapolo ndipo woyenera kufa ndi lupanga adzafa ndi lupanga.+ 12 Nyumba za milungu* ya ku Iguputo ndidzaziwotcha ndi moto.+ Nebukadinezara adzawotcha nyumbazo nʼkutenga milunguyo kupita nayo kudziko lina. Mʼbusa savutika kuvala chovala chake. Mofanana ndi zimenezi, Nebukadinezara sadzavutika kugonjetsa dziko la Iguputo nʼkuchokako mwamtendere.* 13 Iye adzaphwanyaphwanya zipilala za ku Beti-semesi,* mzinda umene uli ku Iguputo. Ndipo nyumba za milungu* ya ku Iguputo adzaziwotcha ndi moto.”’”
44 Mulungu anauza Yeremiya uthenga woti akauze Ayuda onse amene ankakhala mʼdziko la Iguputo,+ mʼmadera a Migidoli,+ Tahapanesi,+ Nofi*+ ndi Patirosi.+ Uthengawo unali wakuti: 2 “Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Inu mwaona masoka onse amene ndinagwetsera Yerusalemu+ ndi mizinda yonse ya Yuda. Lero mizinda imeneyi ndi mabwinja okhaokha ndipo palibe amene akukhalamo.+ 3 Izi zinachitika chifukwa cha zinthu zoipa zimene ankachita nʼkundikhumudwitsa nazo. Iwo ankapitiriza kupereka nsembe+ ndi kutumikira milungu ina imene inuyo, iwowo kapena makolo anu simunkaidziwa.+ 4 Ine ndinkakutumizirani mobwerezabwereza* atumiki anga onse amene ndi aneneri. Ndinkawatuma uthenga wakuti: “Chonde, musachite zinthu zonyansazi zimene ndimadana nazo.”+ 5 Koma sanamvere kapena kutchera khutu lawo kuti asiye kuchita zinthu zoipa zomwe ndi kupereka nsembe kwa milungu ina.+ 6 Choncho ndinasonyeza mkwiyo wanga ndi ukali wanga ndipo unayaka mʼmizinda ya Yuda ndi mʼmisewu ya Yerusalemu moti mizinda imeneyi inakhala mabwinja komanso malo owonongeka ngati mmene zilili lero.’+
7 Tsopano Yehova, Mulungu wa magulu ankhondo akumwamba, Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti, ‘Nʼchifukwa chiyani mukudziitanira tsoka lalikulu? Kodi simukudziwa kuti muphetsa amuna, akazi, ana ndi ana aangʼono mu Yuda, moti sipapezeka aliyense wotsala? 8 Nʼchifukwa chiyani mukufuna kundikhumudwitsa ndi ntchito za manja anu popereka nsembe kwa milungu ina mʼdziko la Iguputo kumene mwapita kuti muzikakhala? Muwonongedwa ndipo aliyense azidzakutembererani ndi kukunyozani pakati pa anthu a mitundu yonse ya padziko lapansi.+ 9 Kodi mwaiwala zoipa zimene makolo anu, mafumu a Yuda+ komanso akazi awo ankachita?+ Kodi mwaiwala zinthu zoipa zimene inuyo ndi akazi anu+ munkachita mʼdziko la Yuda ndi mʼmisewu ya ku Yerusalemu? 10 Iwo sanadzichepetse* mpaka lero, sanasonyeze mantha aliwonse+ kapena kutsatira malamulo ndi malangizo anga amene ndinapatsa inu ndi makolo anu.’+
11 Choncho Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti, ‘Ine ndatsimikiza kukugwetserani tsoka, kuti ndiwononge anthu onse a mu Yuda. 12 Ine ndigwira anthu amene anatsala ku Yuda omwe anatsimikiza mtima kuti apite mʼdziko la Iguputo nʼkumakakhala kumeneko, moti onsewo adzafera mʼdziko la Iguputo.+ Iwo adzaphedwa ndi lupanga komanso adzafa ndi njala. Kuyambira munthu wamba ndi wolemekezeka yemwe, onse adzaphedwa ndi lupanga komanso adzafa ndi njala. Iwo adzakhala otembereredwa, chinthu chochititsa mantha, chinthu chonyozeka ndi chochititsa manyazi.+ 13 Ndidzalanga anthu onse okhala mʼdziko la Iguputo ngati mmene ndinalangira Yerusalemu. Ndidzawalanga ndi lupanga, njala ndi mliri.*+ 14 Ndipo anthu otsala a ku Yuda amene apita kukakhala mʼdziko la Iguputo sadzathawa kapena kupulumuka kuti abwerere kudziko la Yuda. Adzafunitsitsa kubwerera kuti akakhale kumeneko koma sadzabwerera kupatulapo anthu ochepa amene adzathawe.’”
15 Ndiyeno amuna onse amene ankadziwa kuti akazi awo ankapereka nsembe kwa milungu ina, akazi onse amene anaimirira nʼkupanga gulu lalikulu komanso anthu onse amene ankakhala ku Iguputo+ mʼdera la Patirosi,+ anayankha Yeremiya kuti: 16 “Ife sitimvera mawu amene watiuza mʼdzina la Yehova. 17 Mʼmalomwake tichitadi zonse zimene tanena. Tipereka nsembe komanso tithira nsembe zachakumwa kwa Mfumukazi Yakumwamba.*+ Tichita zimenezi mofanana ndi mmene ife, makolo athu, mafumu athu ndi akalonga athu anachitira mʼmizinda ya Yuda ndi mʼmisewu ya Yerusalemu pamene tinkadya mkate nʼkukhuta ndipo zinthu zinkatiyendera bwino, moti sitinaone tsoka lililonse. 18 Ndipotu kungoyambira nthawi imene tinasiya kupereka nsembe ndi kuthira nsembe zachakumwa kwa Mfumukazi Yakumwamba,* tikusowa chilichonse ndipo tawonongeka ndi lupanga komanso njala.”
19 Akaziwo anawonjezera kuti: “Ndipo pamene tinkapereka nsembe ndi kuthira nsembe zachakumwa kwa Mfumukazi Yakumwamba,* kodi amuna athu sanavomereze kuti tipangire Mfumukaziyo makeke oti tikapereke nsembe opangidwa mʼchifanizo chake ndiponso kuti tipereke kwa iye nsembe zachakumwazo?”
20 Kenako Yeremiya anauza anthu onse, amuna ndi akazi awo komanso anthu onse amene ankalankhula naye kuti: 21 “Nsembe zimene inuyo, makolo anu, mafumu anu, akalonga anu ndi anthu amʼdzikolo ankapereka mʼmizinda ya Yuda ndi mʼmisewu ya Yerusalemu,+ Yehova anazikumbukira ndipo zinalowa mumtima mwake. 22 Kenako Yehova sakanathanso kulekerera zinthu zoipa komanso zonyansa zimene munkachita ndipo dziko lanu linasanduka bwinja, chinthu chochititsa mantha ndi chotembereredwa, dziko lopanda munthu wokhalamo ngati mmene ziliri lero.+ 23 Masoka onsewa akugwerani ngati mmene ziliri lero chifukwa chakuti munkapereka nsembe zimenezi komanso chifukwa chakuti munachimwira Yehova. Munachita zimenezi polephera kumvera mawu a Yehova, kutsatira malamulo ake, malangizo ndi zikumbutso zake.”+
24 Ndiyeno Yeremiya anapitiriza kuuza anthu onse ndi akazi onse kuti: “Tamverani mawu a Yehova inu nonse a ku Yuda amene muli ku Iguputo kuno. 25 Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti, ‘Zimene inu ndi akazi anu mwanena mwazikwaniritsadi ndi manja anu chifukwa munanena kuti: “Ife tidzakwaniritsa malonjezo athu akuti tidzapereka nsembe kwa Mfumukazi Yakumwamba* ndi kuti tidzapereka nsembe yachakumwa kwa iye.”+ Akazi inu muchitadi zimene mwalonjeza ndipo mukwaniritsadi malonjezo anu.’
26 Choncho imvani mawu a Yehova, inu nonse a ku Yuda amene mukukhala mʼdziko la Iguputo. Yehova wanena kuti: “Ine ndikulumbira pa dzina langa lalikulu kuti mʼdziko lonse la Iguputo simudzapezeka munthu aliyense wa ku Yuda+ wolumbira mʼdzina langa kuti, ‘Pali Yehova Mulungu wamoyo, Ambuye Wamkulu Koposa!’+ 27 Ine ndine wokonzeka kuwabweretsera tsoka, osati zinthu zabwino.+ Anthu onse a ku Yuda amene ali mʼdziko la Iguputo adzafa ndi lupanga ndiponso njala mpaka atatheratu.+ 28 Anthu ochepa okha adzathawa lupanga mʼdziko la Iguputo nʼkubwerera kudziko la Yuda.+ Ndipo pa nthawiyo, anthu amene anatsala mu Yuda amene anabwera mʼdziko la Iguputo kuti azikhalamo adzadziwa kuti mawu amene akwaniritsidwa ndi a ndani, mawu anga kapena mawu awo.”’”
29 “Yehova wanena kuti: ‘Ndikupatsani chizindikiro chosonyeza kuti ndidzakulangani mʼdziko lino kuti mudziwe kuti mawu anga akuti ndidzakubweretserani tsoka adzakwaniritsidwadi. 30 Yehova wanena kuti: “Ine ndikupereka Farao Hofira, mfumu ya Iguputo, mʼmanja mwa adani ake ndiponso mʼmanja mwa amene akufuna kuchotsa moyo wake, mofanana ndi mmene ndinaperekera Zedekiya mfumu ya Yuda mʼmanja mwa Nebukadinezara* mfumu ya Babulo, amene anali mdani wake komanso amene ankafuna kumupha.”’”+
45 Awa ndi mawu amene mneneri Yeremiya anauza Baruki+ mwana wa Neriya pa nthawi imene Baruki ankalemba mʼbuku mawu amene Yeremiya+ ankamuuza, mʼchaka cha 4 cha ulamuliro wa Yehoyakimu+ mwana wa Yosiya, mfumu ya Yuda. Yeremiya anati:
2 “Ponena za iwe Baruki, Yehova, Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti, 3 ‘Iwe wanena kuti: “Mayo ine! Yehova wawonjezera chisoni pa zopweteka zanga. Ndatopa ndi kubuula ndipo malo ampumulo sindikuwapeza.”’
4 Umuuze kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Taona! Zimene ndamanga ndikuzigwetsa ndipo zimene ndadzala ndikuzizula. Ndichita zimenezi mʼdziko lonse.+ 5 Koma iwe ukufunafuna* zinthu zazikulu. Leka kufunafuna zinthu zimenezo.”’
‘Chifukwa ndatsala pangʼono kubweretsa tsoka pa anthu onse+ ndipo iwe ndidzakupatsa moyo wako* kuti ukhale mphoto yako kulikonse kumene ungapite,’+ akutero Yehova.”
46 Awa ndi mawu amene Yehova anauza mneneri Yeremiya okhudza mitundu ya anthu:+ 2 Uwu ndi uthenga wokhudza Iguputo+ wonena za gulu la asilikali a Farao Neko,+ mfumu ya Iguputo, amene anagonjetsedwa ndi Nebukadinezara* mfumu ya Babulo ku Karikemisi, mʼmbali mwa mtsinje wa Firate. Anagonjetsedwa ndi mfumu imeneyi mʼchaka cha 4 cha ulamuliro wa Yehoyakimu+ mwana wa Yosiya, mfumu ya Yuda. Uthengawo unali wakuti:
3 “Tengani zishango zanu zazingʼono ndi zazikulu,
Ndipo mupite kukamenya nkhondo.
4 Inu okwera pamahatchi, mangani mahatchi anu nʼkukwerapo.
Valani zipewa zanu ndipo mukonzeke.
Pukutani mikondo yanu ingʼonoingʼono ndipo muvale zovala zanu zamamba achitsulo.
5 ‘Nʼchifukwa chiyani akuoneka kuti agwidwa ndi mantha?
Akubwerera ndipo asilikali awo agonjetsedwa.
Iwo athawa mwamantha ndipo asilikali awo sanacheuke.
Zochititsa mantha zili paliponse,’ akutero Yehova.
6 ‘Munthu waliwiro komanso asilikali sangathe kuthawa.
Iwo apunthwa nʼkugwa.
Zimenezi zachitikira kumpoto mʼmphepete mwa mtsinje wa Firate.’+
7 Kodi uyu amene akubwera ngati mtsinje wa Nailo,
Kapena ngati mitsinje ya madzi amphamvu, ndi ndani?
8 Dziko la Iguputo likubwera ngati mtsinje wa Nailo,+
Likubwera ngati mitsinje ya madzi amphamvu,
Ndipo likunena kuti, ‘Ndipita kukaphimba dziko lapansi.
Ndikawononga mzinda ndi onse amene akukhala mumzindawo.’
9 Inu mahatchi pitani.
Inu magaleta thamangani ndi liwiro lalikulu!
Lolani asilikali kuti apite.
Lolani Kusi ndi Puti amene amadziwa kugwiritsa ntchito chishango kuti apite,+
Komanso anthu a ku Ludimu+ amene amadziwa kukunga ndi kuponya uta.+
10 “Limeneli ndi tsiku la Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Ambuye Wamkulu Koposa ndipo ndi tsiku lobwezera chilango kwa adani ake. Lupanga lidzadya adaniwo nʼkukhuta ndipo lidzamwa magazi awo mpaka ludzu lake litatha. Zimenezi zidzachitika chifukwa Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Ambuye Wamkulu Koposa, ali ndi nsembe imene akufuna kupereka mʼdziko lakumpoto, mʼmphepete mwa mtsinje wa Firate.+
11 Iwe namwali, mwana wamkazi wa Iguputo,
Pita ku Giliyadi kuti ukatenge mafuta a basamu.+
Wachulukitsa njira zochiritsira zimene sizinakuthandize,
Chifukwa sunachiritsidwe.+
12 Mitundu ya anthu yamva zochititsa manyazi zimene zakuchitikira,+
Ndipo kulira kwako kwamveka mʼdziko lonse.
Asilikali apunthwitsana,
Ndipo onse agwera limodzi.”
13 Yehova anauza mneneri Yeremiya zokhudza kubwera kwa Nebukadinezara* mfumu ya Babulo kudzaukira dziko la Iguputo. Iye anati:+
14 “Lengezani zimenezi mu Iguputo, muzilengeze ku Migidoli.+
Lengezani zimenezi ku Nofi* ndi ku Tahapanesi.+
Munene kuti, ‘Imani mʼmalo anu ndipo mukhale okonzeka,
Chifukwa lupanga lidzawononga anthu onse amene akuzungulirani.
15 Nʼchifukwa chiyani amuna anu amphamvu akokoloka?
Iwo sanathe kulimba,
Chifukwa Yehova wawagonjetsa.
16 Ambiri akupunthwa ndi kugwa.
Iwo akuuzana kuti:
“Imirirani, tiyeni tibwerere kwa anthu a mtundu wathu ndi kudziko lathu
Chifukwa takumana ndi lupanga loopsa.”’
17 Kumeneko asilikali anu akunena kuti,
‘Farao mfumu ya Iguputo akungoopseza ndi pakamwa chabe
18 ‘Pali ine Mulungu wamoyo,’ yatero Mfumu, imene dzina lake ndi Yehova wa magulu ankhondo akumwamba,
‘Iye* adzabwera nʼkuonekera ngati phiri la Tabori+ pakati pa mapiri ena
Ndiponso ngati phiri la Karimeli+ mʼmphepete mwa nyanja.
19 Longedza katundu wako pokonzekera kupita ku ukapolo,
Iwe mwana wamkazi amene ukukhala mu Iguputo.
Chifukwa mzinda wa Nofi* udzakhala chinthu chochititsa mantha.
Udzawotchedwa ndi moto* ndipo simudzapezeka aliyense wokhalamo.+
20 Iguputo ali ngati ngʼombe yaikazi yooneka bwino imene sinaberekepo,
Koma ntchentche zoluma zidzabwera kuchokera kumpoto kudzamuwononga.
21 Ngakhale asilikali amene wawalemba ganyu ali ngati ana a ngʼombe onenepa,
Koma iwonso abwerera ndipo onse athawa.
22 ‘Iye akuchita phokoso ngati la njoka imene ikuthamanga,
Chifukwa adaniwo amufikira mwamphamvu, atatenga nkhwangwa,
Ngati amuna amene akukagwetsa mitengo.*
23 Iwo adzadula nkhalango yake ngakhale kuti ndi yowirira,’ akutero Yehova.
‘Chifukwa adaniwo ndi ochuluka kwambiri kuposa dzombe ndipo ndi osawerengeka.
24 Mwana wamkazi wa Iguputo adzachititsidwa manyazi.
Iye adzaperekedwa mʼmanja mwa anthu akumpoto.’+
25 Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti: ‘Tsopano ndilanga Amoni+ wa ku No,*+ Farao, Iguputo pamodzi ndi milungu yake+ ndi mafumu ake. Inde ndilanga Farao ndi onse amene amamukhulupirira.’+
26 ‘Ndidzapereka anthu a ku Iguputo mʼmanja mwa anthu amene akufuna moyo wawo, mʼmanja mwa Nebukadinezara* mfumu ya Babulo+ ndi mʼmanja mwa atumiki ake. Koma kenako anthu adzakhalanso mʼdzikolo ngati mmene zinalili kale,’ akutero Yehova.+
27 ‘Koma iwe Yakobo mtumiki wanga, usaope
Ndipo usachite mantha, iwe Isiraeli.+
Chifukwa ndidzakupulumutsa kuchokera kutali.
Ndipo ndidzapulumutsa mbadwa* yako kuchokera mʼdziko limene anali kapolo.+
Yakobo adzabwerera nʼkukhala mwamtendere ndiponso mosatekeseka,
Sipadzakhala wowaopseza.+
28 Choncho, iwe Yakobo mtumiki wanga usachite mantha, chifukwa ine ndili ndi iwe.
47 Yehova anauza mneneri Yeremiya mawu okhudza Afilisiti,+ Farao asanagonjetse mzinda wa Gaza. 2 Yehova wanena kuti:
“Taonani! Madzi akubwera kuchokera kumpoto.
Madzi ake adzakhala mtsinje wosefukira.
Ndipo adzakokolola dziko ndi zonse zimene zili mmenemo.
Adzakokololanso mzinda ndi onse amene akukhala mmenemo.
Amuna adzalira,
Ndipo aliyense amene akukhala mʼdzikolo adzalira mofuula.
3 Abambo adzathawa osayangʼana mʼmbuyo kuti apulumutse ana awo.
Adzachita zimenezi chifukwa manja awo adzafooka,
Akadzamva mgugu wa mahatchi a adani awo,
Akadzamva phokoso la magaleta ankhondo a adani awo
Komanso kulira kwa mawilo ake,
4 Chifukwa tsiku limene likubweralo lidzawononga Afilisiti+ onse.
Lidzawononga aliyense wotsala amene akuthandiza Turo+ ndi Sidoni.+
5 Gaza adzameta mpala chifukwa cha chisoni.
Asikeloni amukhalitsa chete.+
Inu otsala amʼchigwa cha Gaza ndi Asikeloni,
Kodi mupitiriza kudzichekacheka mpaka liti?+
6 Aa! iwe lupanga la Yehova.+
Kodi sukhala chete mpaka liti?
Bwerera mʼchimake.
Upume ndipo ukhale chete.
7 “Kodi lingakhale bwanji chete
Yehova atalilamula?
Walituma kuti likawononge Asikeloni ndi mʼmphepete mwa nyanja.+
Iye walituma kuti lipite kumeneko.”
48 Ponena za Mowabu,+ Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti:
“Tsoka Nebo+ chifukwa wawonongedwa!
Kiriyataimu+ wachititsidwa manyazi ndipo walandidwa.
Malo othawirako otetezeka* achititsidwa manyazi ndipo awonongedwa.+
2 Mowabu sakutamandidwanso.
Ku Hesiboni+ adani amukonzera chiwembu kuti amuwononge ndipo akunena kuti:
‘Bwerani, tiyeni timuwononge kuti asakhalenso mtundu wa anthu.’
Iwenso Madimeni khala chete,
Chifukwa lupanga likukutsatira.
3 Ku Horonaimu+ kwamveka kulira kofuula,
Kwamveka phokoso lachiwonongeko ndi kugwa kwakukulu.
4 Mowabu wawonongedwa.
Ana ake akulira.
5 Anthu akulira mosalekeza pamene akukwera zitunda za Luhiti.
Ndipo panjira yochokera ku Horonaimu akumva anthu akulira mowawidwa mtima chifukwa cha tsoka limene lawagwera.+
6 Thawani, pulumutsani moyo wanu!
Mukhale ngati mtengo wa junipa* mʼchipululu.
7 Chifukwa chakuti mukudalira ntchito zanu ndi chuma chanu,
Inunso mudzagwidwa ndi adani.
Ndipo Kemosi+ adzatengedwa kupita ku ukapolo
Pamodzi ndi ansembe ake ndi akalonga ake.
8 Wowononga adzalowa mumzinda uliwonse,
Ndipo sipadzapezeka mzinda wopulumuka.+
Chigwa chidzawonongedwa,
Chimodzimodzinso malo afulati,* mogwirizana ndi zimene Yehova wanena.
9 Perekani chizindikiro chapamsewu kwa anthu a ku Mowabu,
Chifukwa adzathawa pamene dziko lawo likusanduka bwinja,
Ndipo mizinda yake idzakhala chinthu chochititsa mantha,
Moti simudzapezeka aliyense wokhalamo.+
10 Munthu wozengereza kugwira ntchito imene Yehova wamupatsa ndi wotembereredwa.
Munthu wopewa kukhetsa magazi ndi lupanga lake ndi wotembereredwa.
11 Anthu a ku Mowabu akhala popanda wowasokoneza kuyambira pa unyamata wawo
Ngati vinyo amene nsenga zake zadikha.
Iwo sanatsanulidwepo kuchoka mʼchiwiya china kupita mʼchiwiya china,
Ndipo sanapitepo ku ukapolo.
Nʼchifukwa chake kukoma kwawo sikunasinthe,
Ndipo fungo lawo silinasinthenso.
12 ‘Choncho masiku akubwera,’ akutero Yehova, ‘pamene ndidzawatumizire anthu kuti awapendeketse. Adzawapendeketsa nʼkuwakhuthula ngati vinyo mʼziwiya zawo ndipo adzaswa mitsuko yawo ikuluikulu kukhala mapalemapale. 13 Amowabuwo adzachita manyazi ndi Kemosi, ngati mmene anthu a mʼnyumba ya Isiraeli achitira manyazi ndi Beteli, mzinda umene ankaudalira.+
14 Nʼchifukwa chiyani mukunena kuti: “Ndife asilikali amphamvu, okonzeka kumenya nkhondo”?’+
Ikutero Mfumu, imene dzina lake ndi Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.+
16 Tsoka la Amowabu lili pafupi,
Ndipo nthawi yoti agonjetsedwe ikuyandikira mofulumira kwambiri.+
17 Onse owazungulira adzawamvera chisoni,
Onse amene akudziwa dzina lawo.
Auzeni kuti: ‘Taonani mmene ndodo yamphamvu ndi yokongola ija yathyokera!’
18 Tsika pamalo ako aulemerero
Ndipo ukhale pansi uli ndi ludzu,* iwe mwana wamkazi wokhala ku Diboni+
Chifukwa wowononga Mowabu wabwera kudzakuukira,
Ndipo malo ako a mipanda yolimba kwambiri adzawasandutsa bwinja.+
19 Iwe amene ukukhala ku Aroweli, ima mʼmbali mwa msewu ndipo uone zimene zikuchitika.+
Funsa mwamuna ndi mkazi amene akuthawa kuti, ‘Chachitika nʼchiyani?’
20 Mowabu wachititsidwa manyazi ndipo wagwidwa ndi mantha aakulu.
Lirani mofuula.
Lengezani ku Arinoni+ kuti Mowabu wawonongedwa.
21 Chiweruzo chafika padziko lafulati.*+ Chafika ku Holoni, Yahazi,+ Mefaata,+ 22 Diboni,+ Nebo,+ Beti-dibilataimu, 23 Kiriyataimu,+ Beti-gamuli, Beti-meoni,+ 24 Kerioti,+ Bozira ndi mizinda yonse yamʼdziko la Mowabu, yakutali ndi yapafupi.
25 ‘Mphamvu* za Mowabu zathetsedwa,
Dzanja lake lathyoledwa,’ akutero Yehova.
26 ‘Muledzeretseni+ chifukwa wadzikuza pamaso pa Yehova.+
Mowabu akugubuduka mʼmasanzi ake,
Ndipo wakhala chinthu choyenera kuchinyoza.
27 Kodi kwa inu, Isiraeli sanali chinthu choyenera kunyozedwa?+
Kodi anapezeka pakati pa anthu akuba,
Kuti inu mumupukusire mitu nʼkumamunenera zinthu zoipa?
28 Inu anthu okhala ku Mowabu, chokani mʼmizinda ndipo mukakhale pathanthwe.
Mukhale ngati njiwa imene imamanga chisa chake mʼmbali mwa khomo la phanga.’”
29 “Tamva za kunyada kwa Mowabu. Iye ndi wodzikuza kwambiri.
Tamva za kudzitukumula kwake, kunyada kwake, kudzikweza kwake ndi kudzikuza kwa mtima wake.”+
30 “‘Ine ndikudziwa za mkwiyo wake,’ akutero Yehova,
‘Koma mawu ake opanda pakewo sadzakwaniritsidwa.
Iwo sadzachita chilichonse.
31 Nʼchifukwa chake Mowabu ndidzamulirira,
Mowabu yense ndidzamulirira mofuula
Ndipo ndidzalira maliro a amuna a ku Kiri-haresi.+
Mphukira zako zosangalala zawoloka nyanja.
Zafika kunyanja, ku Yazeri.
33 Kusangalala ndi kukondwera zachotsedwa mʼmunda wa zipatso
Ndiponso mʼdziko la Mowabu.+
Ndachititsa kuti vinyo asiye kutuluka moponderamo mphesa.
Palibe amene adzapondeponde mphesa akufuula mosangalala.
Padzamveka kufuula koma osati kwachisangalalo.’”+
34 “‘Kulira kochokera ku Hesiboni+ kukumveka ku Eleyale.+
Kulira kwawo kukumveka mpaka ku Yahazi,+
Kukumveka kuchokera ku Zowari kukafika ku Horonaimu+ ndi ku Egilati-selisiya.
Ngakhale madzi a ku Nimurimu adzauma.+
35 Ndidzachititsa kuti mʼdziko la Mowabu musapezeke
Munthu aliyense wobweretsa nsembe kumalo okwezeka
Komanso munthu wopereka nsembe kwa mulungu wake,’ akutero Yehova.
36 ‘Nʼchifukwa chake mtima wanga udzalirire* Mowabu ngati chitoliro,*+
Mtima wanga udzalirira* amuna a ku Kiri-haresi ngati chitoliro.*
Chifukwa chuma chimene wapanga chidzawonongeka.
37 Mutu uliwonse wametedwa mpala,+
Ndipo ndevu zonse nʼzometa.
38 Anthu akungolira
Pamadenga onse a nyumba za ku Mowabu
Ndi mʼmabwalo ake onse.
Akulira chifukwa ndaphwanya Mowabu
Ngati chiwiya choyenera kutaidwa,’ akutero Yehova.
39 ‘Taonani, Mowabu wachita mantha kwambiri. Lirani mofuula!
Mowabu wabwerera mwamanyazi.
Mowabu wasanduka chinthu choyenera kunyozedwa,
Komanso chochititsa mantha kwa anthu onse amene amuzungulira.’
40 Yehova wanena kuti:
‘Taonani! Mofanana ndi chiwombankhanga chimene chimatsika nʼkugwira chakudya chake,+
Mdani adzatambasula mapiko ake nʼkugwira Mowabu.+
41 Matauni adzalandidwa,
Ndipo malo ake otetezeka adzalandidwa.
Pa tsiku limenelo, mitima ya asilikali a ku Mowabu
Idzakhala ngati mtima wa mkazi amene akubereka.
42 Mowabu adzawonongedwa ndipo sadzakhalanso mtundu wa anthu,+
Chifukwa wadzikweza pamaso pa Yehova.+
43 Mantha, dzenje ndi msampha zili pa iwe,
Iwe munthu wokhala ku Mowabu,’ akutero Yehova.
44 ‘Aliyense amene akuthawa chifukwa cha mantha adzagwera mʼdzenje,
Ndipo aliyense amene akutuluka mʼdzenjemo adzagwidwa mumsampha.
Chifukwa ndidzapereka chilango kwa anthu a ku Mowabu mʼchaka chimene ndasankha,’ akutero Yehova.
45 ‘Anthu amene akuthawa aima mumthunzi wa Hesiboni ndipo alibe mphamvu.
Chifukwa moto udzachokera ku Hesiboni
Ndipo malawi a moto adzachokera ku Sihoni.+
Motowo udzawotcha Mowabu pachipumi
Komanso mitu ya ana achiwawa.+
46 Tsoka iwe Mowabu!
Anthu a Kemosi+ awonongedwa.
Ana ako aamuna agwidwa ndi adani,
Ndipo ana ako aakazi atengedwa kupita kudziko lina.+
47 Koma mʼmasiku otsiriza ine ndidzasonkhanitsa Amowabu onse amene anagwidwa nʼkutengedwa kupita kudziko lina,’ akutero Yehova.
‘Apa ndi pamene pathera chiweruzo chokhudza Mowabu.’”+
49 Ponena za Aamoni+ Yehova wanena kuti:
“Kodi Isiraeli alibe ana aamuna?
Kodi alibe wolandira cholowa?
Nʼchifukwa chiyani Malikamu+ watenga Gadi+ kuti akhale cholowa chake?
Ndipo nʼchifukwa chiyani anthu ake akukhala mʼmizinda ya Isiraeli?”
2 “‘Choncho taonani! Masiku akubwera,’ akutero Yehova,
‘Amene ndidzachititsa kuti ku Raba,+ umene ndi mzinda wa Aamoni,+ kumveke chizindikiro chakuti kukubwera nkhondo.*
Mzindawu udzasanduka bwinja ndi mulu wadothi.
Midzi yake yozungulira idzawotchedwa ndi moto.’
‘Ndipo Isiraeli adzatenga dziko la anthu amene analanda dziko lake,’+ akutero Yehova.
3 ‘Fuula iwe Hesiboni chifukwa mzinda wa Ai wawonongedwa!
Lirani inu midzi yozungulira Raba.
Valani ziguduli.
Lirani mokuwa nʼkumayendayenda mʼmakola amiyala,*
Chifukwa Malikamu adzatengedwa kupita kudziko lina,
Limodzi ndi ansembe komanso akalonga ake.+
4 Bwanji ukudzitama chifukwa cha zigwa zako,
Zigwa zoyenda madzi, iwe mwana wamkazi wosakhulupirika,
Amene ukudalira chuma chako
Nʼkumanena kuti: “Ndi ndani angabwere kudzandiukira?”’”
5 “Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Ambuye Wamkulu Koposa wanena kuti, ‘Ine ndikukubweretserani chinthu chochititsa mantha,
Kuchokera kwa anthu onse amene akuzungulirani.
Mudzabalalitsidwa kulowera mbali zonse,
Ndipo palibe amene adzasonkhanitse anthu amene athawa.’”
6 “‘Koma pambuyo pake ndidzasonkhanitsa Aamoni amene anatengedwa kupita kudziko lina,’ akutero Yehova.”
7 Ponena za Edomu, Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti:
“Kodi nzeru zinatha ku Temani?+
Kodi anthu ozindikira sakuperekanso malangizo anzeru?
Kodi nzeru zawo zinawola?
8 Thawani! Bwererani!
Pitani kumalo otsika kuti mukakhale kumeneko, inu amene mukukhala ku Dedani!+
Chifukwa Esau ndidzamugwetsera tsoka
Nthawi yoti ndimupatse chilango ikadzafika.
9 Kodi okolola mphesa atabwera kwa iwe,
Sangasiye zina kuti anthu akunkhe?
Ngati akuba atabwera usiku,
Angawononge zokhazo zimene akufuna.+
10 Koma ine ndidzawononga zinthu zonse za Esau nʼkumusiya alibe chilichonse.
Ndidzavundukula malo ake amene amabisalako,
Moti sadzathanso kubisala.
11 Ana anu amasiye asiyeni mʼmanja mwanga,
Ndipo ine ndidzawasiya amoyo,
Akazi anu amasiye adzandikhulupirira.”
12 Yehova wanena kuti: “Taonani! Ngati amene sanapatsidwe chiweruzo kuti amwe zamʼkapu akuyenera kumwa, kodi iweyo ukuyenera kusiyidwa osapatsidwa chilango? Ayi, sudzasiyidwa osapatsidwa chilango chifukwa ukuyenera kumwa zamʼkapumo.”+
13 “Chifukwa ine ndalumbira pa dzina langa kuti Bozira adzakhala chinthu chochititsa mantha,+ adzanyozedwa, adzawonongedwa ndi kutembereredwa ndipo mizinda yake yonse idzakhala mabwinja mpaka kalekale,” akutero Yehova.+
14 Ndamva uthenga wochokera kwa Yehova,
Nthumwi yatumidwa kwa anthu a mitundu ina kukanena kuti:
“Sonkhanani pamodzi nʼkubwera kudzamuukira,
Konzekerani kumenya nkhondo.”+
15 “Taona! Ndakuchititsa kukhala wosafunika pakati pa mitundu ina,
Ndakuchititsa kukhala wonyozeka pakati pa anthu.+
16 Iwe unachititsa kuti anthu azinjenjemera ndipo zimenezi zakupusitsa,
Mtima wako wodzikuza wakupusitsa,
Iwe amene ukukhala mʼmalo obisika amʼthanthwe,
Amene ukukhala paphiri lalitali kwambiri.
Ngakhale kuti unamanga chisa chako pamwamba kwambiri ngati chiwombankhanga,
Ine ndidzakugwetsa kuchoka pamenepo,” akutero Yehova.
17 “Edomu adzakhala chinthu chochititsa mantha.+ Aliyense wodutsa pafupi naye adzamuyangʼanitsitsa mwamantha nʼkumuimbira mluzu chifukwa cha miliri yonse imene idzamugwere. 18 Mofanana ndi mmene Sodomu ndi Gomora komanso midzi imene anali nayo pafupi inawonongedwera, ndi mmenenso zidzakhalire ndi Edomu.+ Palibe aliyense amene adzakhalenso mʼdzikolo,” akutero Yehova.+
19 “Taona! Wina adzabwera ngati mkango+ kuchokera munkhalango zowirira zamʼmphepete mwa Yorodano. Adzabwera kudzaukira malo otetezeka odyetserako ziweto, koma mʼkanthawi kochepa ndidzamuthamangitsa pamalowo. Ndidzaika pamalopo mtsogoleri amene ndamusankha. Chifukwa ndi ndani amene angafanane ndi ine ndipo ndi ndani angatsutsane nane? Kodi pali mʼbusa amene angakane kuchita zimene ine ndikufuna?+ 20 Tsopano amuna inu, tamverani zimene Yehova wasankha* kuchitira Edomu ndiponso zimene waganiza kuti achitire anthu amene akukhala ku Temani:+
Ndithudi, chilombo chidzakokera kutali ana a nkhosa.
Adzachititsa kuti malo awo okhala asanduke bwinja chifukwa cha zimene anthuwo anachita.+
21 Dziko lapansi lagwedezeka chifukwa cha mkokomo wa kugwa kwawo.
Kukumveka kulira!
Kulirako kwamveka mpaka ku Nyanja Yofiira.+
22 Taonani! Mofanana ndi chiwombankhanga mdani adzatsika nʼkugwira chakudya chake,+
Ndipo adzatambasula mapiko ake pa Bozira.+
Pa tsiku limenelo mtima wa asilikali a ku Edomu
Udzakhala ngati mtima wa mkazi amene akubereka.”
23 Uthenga wokhudza Damasiko ndi wakuti:+
“Hamati+ ndi Aripadi achititsidwa manyazi
Chifukwa chakuti amva uthenga woipa.
Iwo agwidwa ndi mantha aakulu.
Nyanja yachita mafunde ndipo singathe kukhala bata.
24 Damasiko sanathenso kulimba mtima.
Watembenuka kuti athawe koma wagwidwa ndi mantha aakulu.
Iye wagwidwa ndi nkhawa ndiponso zowawa,
Ngati mkazi amene akubereka.
25 Kodi zatheka bwanji kuti anthu asachoke mumzinda wotamandika,
Mudzi wobweretsa chisangalalo?
26 Chifukwa anyamata ake adzaphedwa mʼmabwalo ake,
Ndipo asilikali onse adzaphedwa tsiku limenelo,” akutero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.
27 “Mpanda wa Damasiko ndidzauyatsa moto,
Ndipo motowo udzawotcha nsanja zokhala ndi mipanda yolimba za Beni-hadadi.”+
28 Ponena za Kedara+ ndi maufumu a ku Hazori amene Mfumu Nebukadinezara* ya Babulo inawagonjetsa, Yehova wanena kuti:
“Nyamukani, pitani ku Kedara,
Ndipo mukawononge ana a Kumʼmawa.
29 Matenti awo, nkhosa zawo, nsalu za matenti awo
Ndi katundu wawo yense zidzatengedwa.
Ngamila zawo zidzalandidwa,
Ndipo anthu adzawalirira kuti, ‘Zochititsa mantha zili paliponse!’”
30 “Thawani, pitani kutali.
Pitani ndipo mukakhale mʼmalo otsika, inu anthu amene mukukhala ku Hazori,” akutero Yehova.
“Chifukwa Nebukadinezara* mfumu ya Babulo wakonza njira yoti akuukireni,
Ndipo wakonza pulani kuti akugonjetseni.”
31 “Nyamukani, pitani mukaukire mtundu wa anthu umene ukukhala mwamtendere,
Umene ukukhala popanda chosokoneza!” akutero Yehova.
“Kumeneko kulibe zitseko ndi mipiringidzo. Anthu ake amakhala kwaokhaokha.
32 Ngamila zawo zidzalandidwa,
Ndipo ziweto zawo zochulukazo zidzatengedwa ndi adani.
Anthu amene amadulira ndevu zawo zamʼmbali,
Ndidzawabalalitsira kumbali zonse,*+
Ndipo ndizawagwetsera tsoka kuchokera kumadera onse,” akutero Yehova.
33 “Hazori adzakhala malo obisalamo mimbulu,
Adzakhala bwinja mpaka kalekale.
Palibe munthu amene adzakhale kumeneko,
Ndipo palibe aliyense amene adzakhazikike kumeneko.”
34 Yehova anauza Yeremiya mawu okhudza Elamu+ kumayambiriro kwa ulamuliro wa Mfumu Zedekiya+ ya Yuda kuti: 35 “Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti, ‘Ine ndikuthyola uta wa Aelamu,+ umene umachititsa kuti akhale amphamvu.* 36 Anthu a ku Elamu ndidzawabweretsera mphepo 4 kuchokera kumalekezero 4 akumwamba, ndipo ndidzawabalalitsira kumphepo zonsezi. Sipadzapezeka mtundu wa anthu kumene anthu a ku Elamu amene abalalitsidwa sadzapitako.’”
37 “Aelamu ndidzawachititsa mantha pamaso pa adani awo ndi pamaso pa anthu amene akufunafuna moyo wawo. Ndidzawabweretsera tsoka, mkwiyo wanga woyaka moto,” akutero Yehova. “Ndidzawatumizira lupanga mpaka nditawawononga onse.”
38 “Ndidzaika mpando wanga wachifumu ku Elamu+ ndipo kumeneko ndidzawononga mfumu ndi akalonga ake,” akutero Yehova.
39 “Ndiyeno mʼmasiku otsiriza ndidzasonkhanitsa pamodzi anthu a ku Elamu amene anatengedwa kupita kudziko lina,” akutero Yehova.
50 Awa ndi mawu okhudza Babulo,+ dziko la Akasidi, amene Yehova ananena kudzera mwa mneneri Yeremiya. Iye anati:
2 “Nenani ndi kulengeza zimene zachitika kwa anthu a mitundu ina.
Imikani mtengo wachizindikiro ndipo lengezani zimenezi.
Musabise chilichonse.
Nenani kuti, ‘Babulo walandidwa.+
Beli wachititsidwa manyazi.+
Merodaki wachita mantha.
Mafano a Babulo achititsidwa manyazi.
Mafano ake onyansawo* achita mantha.’
3 Chifukwa mtundu wina wa anthu wabwera kudzamuukira kuchokera kumpoto.+
Mtundu umenewu wasandutsa dziko lake kukhala chinthu chochititsa mantha.
Palibe aliyense amene akukhala mʼdzikoli.
Anthu ndiponso ziweto zathawa.
Zathawira kutali.”
4 “Mʼmasiku amenewo ndiponso pa nthawi imeneyo anthu a ku Isiraeli komanso anthu a ku Yuda adzabwera limodzi,”+ akutero Yehova. “Iwo azidzayenda akulira+ ndipo onse pamodzi adzafunafuna Yehova Mulungu wawo.+ 5 Iwo adzafunsira njira yopita ku Ziyoni nkhope zawo zitayangʼana kumeneko.+ Iwo adzanena kuti, ‘Bwerani, tiyeni tikhalenso anthu a Yehova pochita pangano limene lidzakhalapo mpaka kalekale lomwe silidzaiwalika.’+ 6 Anthu anga akhala ngati gulu la nkhosa zosochera.+ Abusa awo ndi amene anawasocheretsa.+ Anawatenga nʼkupita nawo mʼmapiri ndipo ankangowayendetsa kuchoka paphiri kupita pachitunda. Iwo aiwala malo awo opumulirako. 7 Adani awo akawapeza, akumawadya+ ndipo akumanena kuti, ‘Ife tilibe mlandu uliwonse, chifukwa iwo anachimwira Yehova, malo amene chilungamo chimakhalamo. Anachimwira Yehova, chiyembekezo cha makolo awo.’”
8 “Thawani mʼBabulo,
Tulukani mʼdziko la Akasidi,+
Ndipo mukhale ngati mbuzi kapena nkhosa zamphongo zimene zikutsogolera gulu lonse.
9 Inetu ndikuutsa gulu lalikulu la mitundu yamphamvu
Ndi kulibweretsa kuchokera kudziko lakumpoto kuti lidzaukire Babulo.+
Mitunduyi idzabwera ili yokonzeka kumenya nkhondo
Ndipo Babulo adzagonjetsedwa.
10 Adani adzagonjetsa dziko la Kasidi nʼkulitenga.+
Onse amene adzatenge zinthu zamʼdzikoli adzakhutira,”+ akutero Yehova.
Munkadumphadumpha pamsipu ngati ngʼombe yaikazi imene sinaberekepo
Ndipo munkamemesa* ngati mahatchi amphongo.
12 Mayi wanu wachititsidwa manyazi.+
Mayi amene anakuberekani wakhumudwa.
Taonani! Iye ndi wosafunika kwenikweni pakati pa mitundu ina,
Iye ali ngati dera lopanda madzi ndiponso chipululu.+
13 Chifukwa cha mkwiyo wa Yehova, mʼdzikomo simudzakhalanso anthu.+
Dziko lonselo lidzakhala bwinja.+
Aliyense wodutsa pafupi ndi Babulo adzayangʼanitsitsa mwamantha
Ndipo adzamuimbira mluzu chifukwa cha miliri yake yonse.+
14 Bwerani ndi kuzungulira Babulo kumbali zonse muli okonzeka kumenya nkhondo,
Inu nonse amene mumadziwa kukunga uta.
15 Mufuulireni mfuu yankhondo kuchokera kumbali zonse.
Iye wavomereza kuti wagonja.*
Inunso mubwezereni.
Muchitireni zimene iye anakuchitirani.+
16 Iphani munthu amene akufesa mbewu mu Babulo
Ndiponso amene akugwira chikwakwa nthawi yokolola.+
Chifukwa choopa lupanga loopsa, aliyense adzabwerera kwa anthu a mtundu wake,
Aliyense adzathawira kudziko lakwawo.+
17 Anthu a ku Isiraeli ali ngati nkhosa zomwazikana.+ Mikango ndi imene yawabalalitsa.+ Poyamba, mfumu ya Asuri inawadya.+ Kenako Mfumu Nebukadinezara* ya ku Babulo inakukuta mafupa awo.+ 18 Choncho Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti: ‘Ine ndilanga mfumu ya Babulo komanso dziko lake ngati mmene ndinalangira mfumu ya Asuri.+ 19 Isiraeli ndidzamubwezeretsa kumalo ake odyerako msipu+ moti adzadya msipu paphiri la Karimeli ndi ku Basana.+ Ndipo iye adzakhutira mʼmapiri a Efuraimu+ ndi Giliyadi.’”+
20 “Mʼmasiku amenewo ndiponso pa nthawi imeneyo,
Cholakwa cha Isiraeli chidzafufuzidwa,
Koma sichidzapezeka,” akutero Yehova.
“Machimo a Yuda sadzapezeka,
Chifukwa ine ndidzakhululukira anthu amene ndidzawasiye ndi moyo.”+
21 “Pitani mukaukire dziko la Merataimu komanso anthu amene akukhala ku Pekodi.+
Iphani anthu onse nʼkuwawonongeratu,” akutero Yehova.
“Chitani zonse zimene ndakulamulani.
22 Mʼdzikomo mukumveka phokoso lankhondo,
Tsoka lalikulu lawagwera.
23 Taonani! Hamala yophwanyira mitundu ya anthu padziko lonse lapansi yathyoledwa nʼkuwonongedwa.+
Taonani! Babulo wakhala chinthu chochititsa mantha pakati pa anthu a mitundu ina.+
24 Iwe Babulo ndinakutchera msampha ndipo wakodwa,
Koma iwe sunadziwe.
Unapezeka ndi kugwidwa,+
Chifukwa unkalimbana ndi Yehova.
25 Yehova watsegula nyumba yake yosungiramo zida,
Ndipo akutulutsamo zida zimene amagwiritsa ntchito posonyeza mkwiyo wake.+
Chifukwa Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Ambuye Wamkulu Koposa, ali ndi ntchito yoti achite
Mʼdziko la Akasidi.
26 Bwerani mudzamuukire kuchokera mʼmadera akutali.+
Tsegulani nkhokwe zake.+
Muunjikeni pamodzi ngati milu ya tirigu.
Mumuwonongeretu.+
Mʼdzikomo musapezeke aliyense wotsala.
27 Iphani ngʼombe zake zonse zazingʼono zamphongo.+
Zonse zipite kokaphedwa.
Tsoka kwa iwo, chifukwa tsiku lawo lafika,
Nthawi yoti alangidwe yafika.
28 Kukumveka phokoso la anthu amene akuthawa,
Amene apulumuka mʼdziko la Babulo,
Kuti akanene ku Ziyoni kuti Yehova Mulungu wathu akubwezera adani ake.
Akuwabwezera chifukwa cha kuwonongedwa kwa kachisi wake.+
29 Itanani anthu oponya mivi ndi uta kuti adzaukire Babulo,
Anthu onse amene akukunga uta.+
Mangani misasa momuzungulira. Pasapezeke wothawa.
Mubwezereni zimene anachita.+
Muchitireni zonse zimene iye anachita.+
Chifukwa iye wachita zinthu modzikuza pamaso pa Yehova,
Pamaso pa Woyera wa Isiraeli.+
30 Choncho anyamata ake adzaphedwa mʼmabwalo a mizinda yake,+
Ndipo tsiku limenelo asilikali ake onse adzaphedwa,”* akutero Yehova.
31 “Taona! Ine ndikupatsa chilango,+ iwe Babulo wodzikuza,”+ akutero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Ambuye Wamkulu Koposa.
“Chifukwa tsiku lako lifika, nthawi imene ndikuyenera kukupatsa chilango.
32 Iwe Babulo wodzikuza, udzapunthwa nʼkugwa,
Ndipo sipadzapezeka aliyense wokudzutsa.+
Mizinda yako ndidzaiyatsa moto,
Ndipo motowo udzawononga chilichonse chimene chakuzungulira.”
33 Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti:
“Aisiraeli komanso Ayuda akuponderezedwa,
Ndipo anthu onse amene anawagwira nʼkupita nawo kudziko lina akuwakakamira.+
Akukana kuwalola kuti abwerere kwawo.+
34 Koma Wowawombola ndi wamphamvu.+
Dzina lake ndi Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.+
Iye sadzalephera kuwaweruzira mlandu wawo,+
Kuti abweretse mtendere mʼdziko lawo+
Ndi kusokoneza mtendere wa anthu okhala mʼBabulo.”+
35 “Lupanga lidzawononga Akasidi,” akutero Yehova,
“Lidzawononga anthu amene akukhala mʼBabulo, akalonga ake ndi anthu ake anzeru.+
36 Lupanga lidzawononga anthu amene amalankhula zinthu zopanda pake.* Anthu amenewo adzachita zinthu mopanda nzeru.
Lupanga lidzawononga asilikali a mʼBabulo, moti adzachita mantha kwambiri.+
37 Lupanga lidzawononga mahatchi awo, magaleta awo ankhondo
Ndi anthu onse a mitundu yosiyanasiyana amene ali pakati pawo
Ndipo adzakhala ngati akazi.+
Lupanga lidzawononga chuma chake ndipo anthu ena adzachitenga.+
38 Madzi ake adzawonongedwa ndipo adzauma.+
Dziko limeneli ndi la zifaniziro zogoba,+
Ndipo anthu ake amachita zinthu ngati amisala chifukwa cha masomphenya awo ochititsa mantha.
39 Choncho nyama zamʼchipululu zidzakhala mmenemo pamodzi ndi nyama zolira mokuwa,
Ndipo nthiwatiwa zidzakhala mmenemo.+
Mumzindawo simudzakhalanso munthu aliyense,
Ndipo sudzakhala malo oti munthu nʼkukhalamo ku mibadwo yonse.”+
40 “Mofanana ndi mmene Mulungu anawonongera Sodomu ndi Gomora+ komanso midzi imene anali nayo pafupi,+ ndi mmenenso zidzakhalire ndi Babulo. Palibe aliyense amene adzakhalenso mumzindawo,”+ akutero Yehova.
41 “Taona! Mtundu wa anthu ukubwera kuchokera kumpoto.
Mtundu wamphamvu ndi mafumu akuluakulu+ adzakonzekera kuukira
Kuchokera kumadera akutali kwambiri a dziko lapansi.+
42 Iwo amadziwa kuponya mivi ndi uta komanso nthungo.+
Amenewo ndi anthu ankhanza ndipo sadzakumvera chifundo.+
Phokoso lawo lili ngati phokoso la nyanja imene ikuchita mafunde.+
Amachita phokosoli akakwera pamahatchi.
Mogwirizana, iwo ayalana pokonzekera kumenyana nawe, iwe mwana wamkazi wa Babulo.*+
Ikuda nkhawa
Ndipo ikumva zowawa ngati mkazi amene akubereka.
44 Taona! Wina adzabwera ngati mkango kuchokera munkhalango zowirira zamʼmphepete mwa Yorodano. Adzabwera kudzaukira malo otetezeka odyetserako ziweto, koma mʼkanthawi kochepa ndidzawathamangitsa* pamalowo. Ndidzaika pamalopo mtsogoleri amene ndamusankha.+ Chifukwa ndi ndani amene angafanane ndi ine ndipo ndi ndani angatsutsane nane? Kodi pali mʼbusa amene angakane kuchita zimene ine ndikufuna?+ 45 Tsopano amuna inu, tamverani zimene Yehova wasankha* kuchitira Babulo+ ndiponso zimene waganiza kuti achitire dziko la Akasidi.
Ndithudi, chilombo chidzakokera kutali ana a nkhosa.
Adzachititsa kuti malo awo okhala asanduke bwinja chifukwa cha zimene anthuwo anachita.+
46 Phokoso limene lidzamveke Babulo akadzagwidwa lidzachititsa kuti dziko lapansi ligwedezeke,
Ndipo kulira kudzamveka pakati pa mitundu ya anthu.”+
51 Yehova wanena kuti:
2 Ine ndidzatumiza anthu opeta ku Babulo,
Ndipo adzamupeta nʼkusiya dziko lake lili lopanda kanthu.
Pa tsiku la tsoka lake, anthuwo adzamuukira kuchokera kumbali zonse.+
3 Munthu wodziwa kuponya mivi musamulole kukunga uta wake.
Musalole kuti aliyense aimirire atavala chovala chamamba achitsulo.
Anyamata ake musawamvere chisoni.+
Wonongani gulu lake lonse la asilikali.
4 Iwo adzaphedwa mʼdziko la Akasidi,
Adzabayidwa mʼmisewu ya ku Babulo.+
5 Chifukwa Mulungu, Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, sanasiye Isiraeli ndi Yuda kuti akhale akazi amasiye.+
Koma dziko la Akasidi lili ndi mlandu waukulu pamaso pa Woyera wa Isiraeli.
6 Tulukani mʼBabulo nʼkuthawa,
Ndipo pulumutsani moyo wanu.+
Musawonongeke chifukwa cha zolakwa zake.
Ino ndi nthawi yoti Yehova amubwezere.
Mulungu akubwezera Babulo chifukwa cha zimene anachita.+
7 Babulo anali ngati kapu yagolide mʼdzanja la Yehova.
Anachititsa kuti dziko lonse lapansi liledzere.
Mitundu ya anthu yaledzera ndi vinyo wake.+
Nʼchifukwa chake mitundu ya anthu ikuchita zinthu ngati anthu amisala.+
8 Babulo wagwa mwadzidzidzi ndipo wasweka.+
Mulirireni mofuula.+
Mʼpatseni mafuta a basamu kuti ululu wake uthe, mwina angachire.”
9 “Tinayesetsa kuti tichiritse Babulo koma sanachiritsike.
Musiyeni, tiyeni tizipita. Aliyense apite kudziko lakwawo.+
Chifukwa zolakwa zake zafika kumwamba,
Zafika pamwamba kwambiri ngati mitambo.+
10 Yehova watichitira zinthu zachilungamo.+
Bwerani, tiyeni tinene mu Ziyoni ntchito za Yehova Mulungu wathu.”+
11 “Nolani mivi yanu.*+ Tengani zishango zozungulira.
Yehova akubwezera Babulo, akumubwezera chifukwa cha kachisi wake.
12 Kwezani chizindikiro+ kuti muukire mpanda wa Babulo.
Wonjezerani alonda ndipo ikani alondawo pamalo awo.
Uzani omenya nkhondo mobisalira anzawo kuti akonzeke.
Chifukwa Yehova waganiza zoti achite,
Ndipo adzachitira anthu amene akukhala ku Babulo zimene ananena.”+
13 “Iwe mkazi amene ukukhala pamadzi ambiri,+
Amene uli ndi chuma chambiri,+
Mapeto ako afika ndipo nthawi yako yopanga phindu yatha.+
14 Yehova wa magulu ankhondo akumwamba walumbira mʼdzina lake kuti,
‘Mʼdziko lako ndidzadzazamo amuna ochuluka ngati dzombe,
Ndipo amunawo adzafuula mosangalala chifukwa chakuti akugonjetsa.’+
15 Iye ndi Mulungu amene anapanga dziko lapansi pogwiritsa ntchito mphamvu zake,
Amene anakhazikitsa dziko lapansi pogwiritsa ntchito nzeru zake+
Amenenso anatambasula kumwamba chifukwa cha kuzindikira kwake.+
16 Mawu ake akamveka,
Madzi akumwamba amachita mkokomo,
Ndipo amachititsa mitambo* kukwera kuchokera kumalekezero a dziko lapansi.
Iye amachititsa kuti kukamagwa mvula mphezi zizingʼanima
Ndipo amatulutsa mphepo mʼnyumba zake zosungira.+
17 Munthu aliyense akuchita zinthu mopanda nzeru komanso mosazindikira.
Mmisiri wa zitsulo aliyense adzachita manyazi chifukwa cha chifaniziro chake chosula.+
Chifukwa chifaniziro chake chopangidwa ndi chitsulo chosungunula ndi mulungu wonama
18 Iwo ndi achabechabe,+ oyenera kunyozedwa.
Tsiku loti aweruzidwe likadzafika adzawonongedwa.
19 Koma Mulungu, amene ndi cholowa cha Yakobo, sali ngati mafano amenewa,
Chifukwa iye ndi amene anapanga chilichonse,
Ngakhalenso ndodo ya cholowa chake.+
Dzina lake ndi Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.”+
20 “Iwe ndiwe chibonga changa, chida changa chomenyera nkhondo,
Ndipo ndidzakugwiritsa ntchito pophwanya mitundu ya anthu.
Ndidzakugwiritsa ntchito powononga maufumu.
21 Ndidzakugwiritsa ntchito pophwanya hatchi ndi wokwerapo wake.
Ndidzakugwiritsa ntchito pophwanya magaleta ankhondo ndi okweramo ake.
22 Ndidzakugwiritsa ntchito pophwanya mwamuna ndi mkazi.
Ndidzakugwiritsa ntchito pophwanya mwamuna wachikulire ndi kamnyamata.
Ndidzakugwiritsa ntchito pophwanya mnyamata ndi mtsikana.
23 Ndidzakugwiritsa ntchito pophwanya mʼbusa ndi ziweto zake.
Ndidzakugwiritsa ntchito pophwanya mlimi ndi ziweto zimene amazigwiritsa ntchito polima.
Ndidzakugwiritsa ntchito pophwanya abwanamkubwa ndi achiwiri kwa olamulira.
24 Ndidzabwezera Babulo ndi anthu onse amene akukhala mʼdziko la Kasidi
Chifukwa cha zoipa zonse zimene anachita ku Ziyoni inu mukuona,”+ akutero Yehova.
25 “Ine ndidzachita nawe nkhondo,+ iwe phiri lowononga
Amene wawononga dziko lonse lapansi,” akutero Yehova.+
“Ndidzatambasula dzanja langa nʼkukupatsa chilango moti ndidzakugubuduza kuchokera pamatanthwe
Ndipo ndidzakusandutsa phiri limene lawotchedwa ndi moto.”
26 “Anthu sadzatenga kwa iwe mwala wapakona kapena mwala wapamaziko,
Chifukwa udzakhala bwinja mpaka kalekale,”+ akutero Yehova.
27 “Kwezani chizindikiro mʼdzikoli.+
Imbani lipenga pakati pa mitundu ya anthu.
Sankhani* mitundu ya anthu kuti ichite naye nkhondo.
Muitanireni maufumu a ku Ararati,+ ku Mini ndi ku Asikenazi+ kuti adzamuukire.
Muikireni wolemba anthu usilikali.
Mubweretsereni mahatchi ambiri ngati dzombe lingʼonolingʼono.
28 Sankhani* mitundu ya anthu kuti ichite naye nkhondo.
Sankhani mafumu a ku Mediya,+ abwanamkubwa ake ndi achiwiri kwa olamulira awo onse
Komanso mayiko onse amene iwo amawalamulira.
29 Dziko lidzagwedezeka ndi kunjenjemera,
Chifukwa Yehova adzachitira Babulo zimene akuganiza
Kuti dziko la Babulo likhale chinthu chochititsa mantha, lopanda munthu wokhalamo.+
30 Asilikali a ku Babulo asiya kumenya nkhondo.
Iwo akhala pansi mʼmalo awo otetezeka.
Mphamvu zawo zatha.+
Akhala ngati akazi.+
Nyumba za mʼBabulo zawotchedwa.
Mipiringidzo yake yathyoledwa.+
31 Munthu amene watumidwa kukanena uthenga wakumana ndi mnzake,
Ndipo mthenga wina wakumana ndi mnzake.
Onsewa akukanena kwa mfumu ya Babulo kuti mzinda wake walandidwa kumbali zonse.+
32 Akukanena kuti malo owolokera mtsinje alandidwa,+
Ngalawa zagumbwa* zawotchedwa
Komanso kuti asilikali akuchita mantha kwambiri.”
33 Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Mulungu wa Isiraeli wanena kuti:
“Mwana wamkazi wa Babulo* ali ngati malo opunthira mbewu.
Ino ndi nthawi yomupondaponda.
Posachedwapa nthawi yokolola imufikira.”
Wandisandutsa chiwiya chopanda kanthu.
Wandimeza ngati chinjoka chachikulu.+
Wakhuta zinthu zanga zabwino.
Wanditsukuluza.
35 Anthu amene akukhala mu Ziyoni akunena kuti, ‘Chiwawa chimene anachitira ine ndi thupi langa chigwerenso Babulo.’+
Ndipo Yerusalemu akunena kuti, ‘Magazi anga akhale pa anthu amene akukhala mʼdziko la Kasidi.’”
36 Choncho Yehova wanena kuti:
Ndidzaphwetsa nyanja yake ndi zitsime zake.+
37 Babulo adzakhala milu yamiyala,+
Malo obisalamo mimbulu,+
Chinthu chochititsa mantha komanso chimene anthu azidzachiimbira mluzu
Ndipo simudzapezeka munthu wokhalamo.+
38 Anthu onse pamodzi adzabangula ngati mikango yamphamvu.*
Adzalira ngati ana a mikango.”
39 “Akadzakhala ndi chilakolako champhamvu chofuna kudya, ndidzawakonzera phwando ndipo ndidzawaledzeretsa
Nʼcholinga choti asangalale.+
Kenako adzagona tulo tosatha
Ndipo sadzadzukanso,”+ akutero Yehova.
40 “Ndidzapita nawo kumalo okawaphera ngati ana a nkhosa,
Ngati nkhosa zamphongo pamodzi ndi mbuzi.”
Babulo wakhala chinthu chochititsa mantha pakati pa mitundu ya anthu.
42 Nyanja yasefukira nʼkumiza Babulo.
Mzinda wa Babulo wamizidwa ndi mafunde ambiri a nyanjayo.
43 Mizinda yake yakhala chinthu chochititsa mantha, dziko lopanda madzi komanso chipululu.
Mizindayo yakhala dziko limene simudzakhalanso munthu aliyense ndipo palibe munthu amene adzadutsemo.+
Mitundu ya anthu sidzapitanso kwa iye,
Ndipo mpanda wa Babulo udzagwa.+
45 Tulukani mʼBabulo anthu anga.+
Thawani mkwiyo wa Yehova+ woyaka moto kuti mupulumutse moyo wanu.+
46 Musataye mtima kapena kuchita mantha ndi uthenga umene udzamveke mʼdzikoli.
Mʼchaka chimodzi uthenga udzafika,
Kenako mʼchaka chotsatira kudzabweranso uthenga wina,
Wonena za chiwawa chimene chidzachitike mʼdzikoli komanso wonena kuti wolamulira akuukira wolamulira mnzake.
47 Choncho masiku adzafika
Pamene ndidzawononge zifaniziro zogoba za ku Babulo.
Dziko lake lonse lidzachititsidwa manyazi,
Ndipo mitembo ya anthu ake onse amene adzaphedwe idzakhala paliponse mumzindawo.+
48 Kumwamba ndi dziko lapansi komanso chilichonse cha mmenemo
Zidzafuula mosangalala poona kuti Babulo wagwa,+
Chifukwa owononga adzabwera kwa iye kuchokera kumpoto,”+ akutero Yehova.
49 “Babulo sanaphetse anthu a mu Isiraeli okha+
Koma anaphetsanso anthu apadziko lonse lapansi ku Babuloko.
50 Inu amene mwathawa lupanga, pitirizani kuthawa, musaime.+
Kumbukirani Yehova pamene muli kutali kwambiri,
Ndipo muziganizira Yerusalemu mumtima mwanu.”+
51 “Tachititsidwa manyazi chifukwa tamva mawu onyoza.
Manyazi aphimba nkhope zathu,
Chifukwa anthu achilendo* abwera kudzaukira malo oyera a mʼnyumba ya Yehova.”+
52 “Choncho masiku adzafika,” akutero Yehova,
“Pamene ndidzawononge zifaniziro zake zogoba,
Ndipo mʼdziko lake lonse anthu ovulazidwa adzakhala akubuula.”+
53 “Ngakhale Babulo atakwera kukafika kumwamba,+
Ngakhale atalimbitsa kwambiri mpanda wake wautaliwo,
Anthu amene adzamuwononge adzabwera kuchokera kwa ine,”+ akutero Yehova.
54 “Tamverani! Ku Babulo kukumveka kulira kofuula,+
Mʼdziko la Akasidi mukumveka phokoso la chiwonongeko chachikulu,+
55 Chifukwa Yehova akuwononga Babulo,
Adzachititsa kuti mawu ake aakuluwo asamvekenso,
Ndipo phokoso la adani ake lidzakhala ngati la mafunde amphamvu.
Phokoso la mawu awo lidzamveka.
56 Wowononga adzafikira Babulo.+
Asilikali ake adzagwidwa,+
Mauta awo adzathyoledwa,
Chifukwa Yehova ndi Mulungu amene amapereka chilango choyenera.+
Iye adzabwezera ndithu.+
57 Ndidzaledzeretsa akalonga ake, anthu ake anzeru,+
Abwanamkubwa ake, achiwiri kwa olamulira ake ndi asilikali ake,
Ndipo adzagona tulo tosatha,
Moti sadzadzukanso,”+ ikutero Mfumu, imene dzina lake ndi Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.
58 Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti:
“Ngakhale kuti mpanda wa Babulo ndi waukulu, wonse udzagwetsedwa,+
Ndipo ngakhale kuti mageti ake ndi ataliatali, adzawotchedwa.
Anthu adzagwira ntchito yotopetsa pachabe.
Mitundu ya anthu idzadzitopetsa ndi ntchito, koma ntchito yawoyo idzawonongedwa ndi moto.”+
59 Mneneri Yeremiya anapereka malangizo kwa Seraya mwana wa Neriya+ mwana wa Maseya. Anapereka malangizowo pamene Seraya anapita ndi Zedekiya mfumu ya Yuda ku Babulo mʼchaka cha 4 cha ufumu wake. Seraya anali woyangʼanira zinthu za mfumu. 60 Yeremiya analemba mʼbuku limodzi masoka onse amene adzagwere Babulo. Iye analemba mawu onsewa okhudza zimene zidzachitikire Babulo. 61 Choncho Yeremiya anauza Seraya kuti: “Ukakafika ku Babulo nʼkuona mzindawo, ukawerenge mokweza mawu onsewa. 62 Kenako ukanene kuti, ‘Inu Yehova! Inu mwanena kuti malo ano adzawonongedwa ndipo simudzapezeka aliyense wokhalamo, munthu kapena nyama, komanso kuti mzindawu udzakhala bwinja mpaka kalekale.’+ 63 Ndiye ukakamaliza kuwerenga bukuli, ukalimangirire mwala nʼkuliponya pakati pa mtsinje wa Firate. 64 Ndiyeno ukanene kuti, ‘Umu ndi mmene Babulo adzamirire ndipo sadzatulukanso+ chifukwa cha tsoka limene ndikumugwetsera. Ndipo anthu amene akukhala mumzindawo adzatopa.’”+
Mawu a Yeremiya athera pamenepa.
52 Zedekiya+ anayamba kulamulira ali ndi zaka 21 ndipo analamulira zaka 11 ku Yerusalemu. Mayi ake anali a ku Libina ndipo dzina lawo linali Hamutali+ mwana wa Yeremiya. 2 Zedekiya anapitiriza kuchita zoipa pamaso pa Yehova, mogwirizana ndi zonse zimene Yehoyakimu anachita.+ 3 Zinthu zimenezi zinachitika ku Yerusalemu ndi ku Yuda chifukwa Yehova anakwiya kwambiri mpaka anawachotsa pamaso pake.+ Kenako Zedekiya anagalukira mfumu ya Babulo.+ 4 Mʼchaka cha 9 cha ufumu wa Zedekiya, mʼmwezi wa 10, pa tsiku la 10 la mweziwo, Nebukadinezara* mfumu ya Babulo anabwera ku Yerusalemu pamodzi ndi asilikali ake onse. Anabwera kudzamenyana ndi anthu amumzindawo ndipo anamanga msasa komanso mpanda kuzungulira mzinda wonsewo.+ 5 Mzindawo unazunguliridwa mpaka chaka cha 11 cha Mfumu Zedekiya.
6 Mʼmwezi wa 4, pa tsiku la 9,+ njala inafika poipa kwambiri mumzindawo ndipo anthu analibiretu chakudya.+ 7 Pamapeto pake, mpanda wa mzindawo unabooledwa ndipo asilikali onse anathawa mumzindawo usiku kudzera pageti limene linali pakati pa makoma awiri, pafupi ndi munda wa mfumu. Akasidi anali atazungulira mzindawo ndipo iwo anapitiriza kuthawa kulowera cha ku Araba.+ 8 Koma asilikali a Akasidi anayamba kuthamangitsa Zedekiya+ ndipo anamupeza mʼchipululu cha Yeriko. Zitatero asilikali onse a mfumuyo anabalalika nʼkuisiya yokha. 9 Kenako Akasidiwo anagwira mfumuyo nʼkupita nayo ku Ribila kwa mfumu ya Babulo mʼdziko la Hamati ndipo anaipatsa chigamulo. 10 Ndipo mfumu ya Babulo inapha ana aamuna a Zedekiya, iye akuona. Inaphanso akalonga onse a ku Yuda ku Ribila komweko. 11 Kenako mfumu ya Babulo inachititsa khungu Zedekiya,+ inamumanga ndi maunyolo akopa* nʼkupita naye ku Babulo ndipo inamuika mʼndende mpaka tsiku la imfa yake.
12 Mʼmwezi wa 5, pa tsiku la 10 la mweziwo, chomwe chinali chaka cha 19 cha Mfumu Nebukadinezara* ya ku Babulo, Nebuzaradani mkulu wa asilikali olondera mfumu, amene anali mtumiki wa mfumu ya Babulo, anabwera ku Yerusalemu.+ 13 Iye anatentha nyumba ya Yehova,+ nyumba ya mfumu, nyumba iliyonse yaikulu komanso nyumba zonse za mu Yerusalemu. 14 Kenako asilikali onse a Akasidi, omwe anali ndi mkulu wa asilikali olondera mfumu uja, anagwetsa mpanda wonse wa Yerusalemu.+
15 Nebuzaradani mkulu wa asilikali olondera mfumu anatenga ena mwa anthu onyozeka ndiponso anthu ena onse amene anatsala mumzindawo. Anatenganso anthu amene anathawira kwa mfumu ya Babulo komanso amisiri onse aluso nʼkupita nawo ku ukapolo.+ 16 Ena mwa anthu osauka kwambiri amʼdzikolo, Nebuzaradani mkulu wa asilikali olondera mfumu uja anawasiya kuti akhale olima minda ya mpesa ndi anthu ogwira ntchito mokakamizidwa.+
17 Akasidi anaphwanyaphwanya zipilala zakopa+ zapanyumba ya Yehova, zotengera zokhala ndi mawilo+ ndiponso thanki yakopa yosungira madzi+ zimene zinali mʼnyumba ya Yehova nʼkutenga kopa yense kupita naye ku Babulo.+ 18 Akasidiwo anatenganso ndowa, mafosholo, zozimitsira nyale, mbale zolowa,+ makapu+ ndi ziwiya zonse zakopa zimene ansembe ankagwiritsa ntchito potumikira mʼkachisi. 19 Mkulu wa asilikali olondera mfumu uja anatenga mabeseni,+ zopalira moto, mbale zolowa, ndowa zochotsera phulusa, zoikapo nyale,+ makapu ndi mbale zinanso zolowa zomwe zinali zagolide komanso zasiliva weniweni.+ 20 Koma zinali zosatheka kuyeza kulemera kwa kopa wa zipilala ziwiri zija, thanki yosungira madzi, ngʼombe zakopa 12+ zimene zinali pansi pa thanki yosungira madzi ndiponso zotengera zokhala ndi mawilo zimene Mfumu Solomo anapanga kuti zizigwira ntchito panyumba ya Yehova chifukwa anali wochuluka kwambiri.
21 Ponena za zipilalazo, chipilala chilichonse chinali chachitali mamita 8* ndipo chinkatha kuzunguliridwa ndi chingwe chachitali mamita 5.*+ Chipilala chilichonse chinali ndi mphako mkati ndipo kuchindikala kwake kunali masentimita 7.* 22 Mutu wa chipilala chilichonse unali wakopa. Mutuwo unali wautali mamita awiri*+ ndipo maukonde ndi makangaza* amene anazungulira mutuwo, onse anali akopa. Chipilala chachiwiri chinali chofanana ndi choyambacho, chimodzimodzinso makangaza ake. 23 Makangaza amene anali mʼmbali mwa zipilalazo analipo 96 ndipo makangaza onse amene anazungulira maukondewo analipo 100.+
24 Mkulu wa asilikali olondera mfumu uja anatenganso Seraya+ wansembe wamkulu, Zefaniya+ wansembe wachiwiri ndi alonda atatu apakhomo.+ 25 Mumzindawo anatengamonso nduna imodzi yapanyumba ya mfumu imene inkayangʼanira asilikali. Anatenganso anzake 7 a mfumu amene anawapeza mumzindawo. Komanso anatenga mlembi wa mkulu wa asilikali yemwe ankasonkhanitsa anthu ndiponso amuna 60 mwa anthu wamba amene anawapeza mumzindawo. 26 Nebuzaradani mkulu wa asilikali olondera mfumu anatenga anthuwa nʼkupita nawo ku Ribila kwa mfumu ya Babulo. 27 Mfumu ya Babuloyo inapha anthuwo ku Ribila+ mʼdziko la Hamati. Choncho Ayuda anatengedwa kudziko lawo nʼkupita nawo ku ukapolo.+
28 Chiwerengero cha anthu amene Nebukadinezara* anawatenga kupita nawo ku ukapolo ndi ichi: mʼchaka cha 7 cha ulamuliro wake, anatenga Ayuda 3,023.+
29 Mʼchaka cha 18 cha ulamuliro wa Nebukadinezara,*+ anthu 832 anatengedwa kuchokera ku Yerusalemu.
30 Mʼchaka cha 23 cha ulamuliro wa Nebukadinezara,* Nebuzaradani mkulu wa asilikali olondera mfumu anatenga Ayuda 745 kupita nawo ku ukapolo.+
Anthu onse amene anatengedwa kupita ku ukapolo anali 4,600.
31 Kenako mʼchaka cha 37 cha ukapolo wa Yehoyakini+ mfumu ya Yuda, Evili-merodaki anakhala mfumu ya Babulo. Ndiyeno mʼchaka chomwecho mʼmwezi wa 12, pa tsiku la 25 la mweziwo, iye anamasula* Yehoyakini mfumu ya Yuda nʼkumutulutsa mʼndende.+ 32 Ankalankhula naye mokoma mtima ndipo anakweza mpando wake wachifumu kuposa mipando ya mafumu ena amene anali naye ku Babulo. 33 Choncho Yehoyakini anavula zovala zake zakundende ndipo ankadya limodzi ndi mfumuyo masiku onse a moyo wake. 34 Tsiku lililonse ankapatsidwa chakudya kuchokera kwa mfumu ya Babulo, kwa moyo wake wonse mpaka tsiku limene anafa.
Nʼkutheka kuti dzinali limatanthauza kuti “Yehova Amakweza.”
Kapena kuti, “ndinakusankha.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “usanatuluke mʼmimba.”
Kapena kuti, “ndinakupatula.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “nthambi ya wochititsa kukhala maso.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “umene aukupizira,” kusonyeza kuti moto umene uli pansi pa mphikawo ukuyaka kwambiri.
Mʼchilankhulo choyambirira, “umange mʼchiuno mwako.”
Kapena kuti, “amkuwa.”
Kapena kuti, “Ndikukumbukira bwino chikondi chokhulupirika chimene unkasonyeza.”
Kapena kuti, “agoba.” Nʼkutheka kuti achita zimenezi pamiyala.
Kapena kuti, “mikango yaingʼono yamanyenje.”
Kapena kuti, “ku Memfisi.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “anakudya paliwombo.”
Umenewu ndi mtsinje umene unatuluka mumtsinje wa Nailo.
Mʼchilankhulo choyambirira, “mwezi woti.”
Kapena kuti, “ndi milungu yachilendo.”
Mawu amʼchilankhulo choyambirira amene amasuliridwa kuti “chilango” ali ndi matanthauzo ambiri. Akhoza kutanthauza malangizo, kuphunzitsa, kudzudzula, kulimbikitsa, kulanga kapena uphungu.
Kapena kuti, “lamba wovala pa tsiku laukwati.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Mluya.”
Kapena kuti, “ndi milungu yachilendo.”
Mabaibulo ena amati, “mwamuna wanu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “pakati pa asilikali a mitundu ya anthu.”
Kapena kuti, “Koma mulungu wochititsa manyazi wadya.”
Kapena kuti, “pamene lupanga latibaya mumtima.”
“Mankhusu” ndi makoko amene amachotsa ku mbewu ngati mpunga popuntha ndipo amatha kuwauluza ndi mphepo.
Mʼchilankhulo choyambirira, “Oona zochitika.” Amenewa ndi anthu amene ankaona zimene zikuchitika mumzinda kuti adziwe nthawi yoyenera kuukira mzindawo.
Mʼchilankhulo choyambirira, “Mʼmatumbo mwanga ine.”
Mabaibulo ena amati, “Mfuwu ya nkhondo.”
Kapena kuti, “anzeru.”
Kapena kuti, “Ndipo sindidzamva chisoni.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “zovala zofiira,” kutanthauza zovala zofiira zamtengo wapatali.
Mawu akuti “mwana wamkazi wa Ziyoni” ndi mawu a ndakatulo ndipo nthawi zambiri amanena za mzinda wa Yerusalemu kapena anthu amene ankakhala mumzindawo.
Mʼchilankhulo choyambirira, “sanafooke.”
Mawu akuti “kumemesa” amatanthauza zimene nyama yamphongo imachita ikafuna kukwera.
Mabaibulo ena amati, “Iye kulibe.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “inu anthu opusa opanda mtima.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼmilungu yoikidwiratu.”
Mawu akuti “mwana wamkazi wa Ziyoni” ndi mawu a ndakatulo ndipo nthawi zambiri amanena za mzinda wa Yerusalemu kapena anthu amene ankakhala mumzindawo.
Mʼchilankhulo choyambirira, “Dziyeretseni.”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mʼchilankhulo choyambirira, “Makutu awo sanawachite mdulidwe.”
Kapena kuti, “mwachinyengo fupa lothyoka la anthu anga.”
Kapena kuti, “Ndipo anakana malangizo anga.”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Apa akunena Yeremiya.
Kapena kuti, “mkuwa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Nyumba izi,” kutanthauza nyumba zonse zimene zinali pakachisi.
Kapena kuti, “nsembe zautsi.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ngakhale kuti ndinkadzuka mʼmamawa nʼkulankhula nanu.”
Limeneli ndi dzina laulemu la mulungu wamkazi amene Aisiraeli opanduka ankamulambira. Iwo ankakhulupirira kuti ameneyu ndi mulungu amene ankathandiza akazi kuti azibereka.
Mʼchilankhulo choyambirira, “Tsiku lililonse ndinkadzuka mʼmamawa nʼkuwatumiza.”
Mawu amʼchilankhulo choyambirira amene amasuliridwa kuti “malangizo” ali ndi matanthauzo ambiri. Akhoza kutanthauza malangizo, kuphunzitsa, kudzudzula, kulimbikitsa, kulanga, kapena uphungu.
Mʼchilankhulo choyambirira, “ndipo kukhulupirika kwachotsedwa mʼkamwa mwawo.”
Kapena kuti, “tsitsi lomwe ndi chizindikiro cha kudzipereka.”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena, “Gehena.”
Kapena kuti, “chimene sichinabwerepo mʼmaganizo mwangamu.”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena, “Gehena.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ndi pamagulu onse ankhondo akumwamba.”
Kapena kuti, “nthawi yochoka dera lina kupita dera lina.”
Kapena kuti, “malangizo a Yehova.”
Kapena kuti, “kuchiritsa mwachinyengo fupa lothyoka la mwana wamkazi.”
Mawu akuti “kumemesa” amatanthauza zimene nyama yamphongo imachita ikafuna kukwera.
Kapena kuti, “dokotala.”
Kapena kuti, “malangizo anga amene ndinawapatsa.”
Kapena kuti, “sompho wake.” Sompho ndi chida chimene mʼmadera ena amanena kuti kasemasema.
Vesi 11 poyamba linalembedwa mʼChiaramu.
Kapena kuti, “nthunzi.”
Kapena kuti, “mpweya.”
Kapena kuti, “Pa nthawi ino ndikutayira kutali.”
Kapena kuti, “chifukwa fupa langa lathyoka.”
Zikuoneka kuti apa amauza Yeremiya.
Mʼchilankhulo choyambirira, “Ame.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Ndinkadzuka mʼmawa kwambiri nʼkuwalangiza.”
Kapena kuti, “Ndipo mulungu wochititsa manyazi mwamumangira.”
Apa akunena Yeremiya.
Zimenezi ndi nsembe zimene ankapereka kukachisi.
Kapena kuti, “Amafufuza mmene ndikumvera mumtima.” Mʼchilankhulo choyambirira, “impso.”
Kapena kuti, “mmene akumvera mumtima mwawo.” Mʼchilankhulo choyambirira, “impso zawo zili kutali.”
Mabaibulo ena amati, “chikundilirira.”
Kapena kuti, “Mizinda yakumʼmwera yazunguliridwa ndi adani.”
Kapena kuti, “munthu wa ku Itiyopiya.”
Mawu akuti “kumemesa” amatanthauza zimene nyama yamphongo imachita ikafuna kukwera.
Kapena kuti, “lochititsa manyazi.”
Kapena kuti, “matenda.”
Mabaibulo ena amati, “ziweruzo zamitundu 4.” Mʼchilankhulo choyambirira, “mabanja 4.”
Mabaibulo ena amati, “Ukupitiriza kuyenda chafutambuyo.”
Kapena kuti, “Ndatopa ndi kusintha maganizo.”
Mabaibulo ena amati, “Dzuwa lachita manyazi ndipo lathedwa nzeru.”
Kapena kuti, “mkuwa.”
Kapena kuti, “uthenga wachiweruzo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Ndipo udzaima pamaso panga.”
Kapena kuti, “Udzakhala wondilankhulira.”
Zikuoneka kuti imeneyi inali miyambo ya maliro imene Aisiraeli opanduka ankachita.
Mʼchilankhulo choyambirira, “maso anga ali pa njira zawo zonse.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mitembo ya mafano.”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mabaibulo ena amati, “Chifukwa mwayatsidwa ndi mkwiyo wanga ngati moto.”
Kapena kuti, “wachinyengo.”
Mabaibulo ena amati, “ndipo ndi wosachiritsika.”
Kapena kuti, “Ndimafufuza mmene munthu akumvera mumtima.” Mʼchilankhulo choyambirira, “impso.”
Kapena kuti, “amapeza chuma koma osati mwachilungamo.”
Kapena kuti, “komanso muwawononge kuwirikiza kawiri.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “anaumitsa khosi lawo.”
Kapena kuti, “kuchokera kumʼmwera.”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Kapena kuti, “chipale chofewa chamʼmapiri a ku Lebanoni chimasungunuka.”
Kapena kuti, “nsembe zautsi.”
Kapena kuti, “zosalimidwa.”
Kapena kuti, “malangizo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “tiyeni timumenye ndi lilime.”
Kapena kuti, “aumitsa nkhosi lawo kuti asamvere.”
Kapena kuti, “Mwandidabwitsa.”
Kapena kuti, “Mumaona mmene munthu akumvera mumtima.” Mʼchilankhulo choyambirira, “Mumaona impso za munthu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Nebukadirezara.” Kameneka ndi kalembedwe kena ka dzinali.
Kapena kuti, “matenda aakulu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Nebukadirezara.” Kameneka ndi kalembedwe kena ka dzinali.
Mʼchilankhulo choyambirira, “Nkhope yanga ili pa mzinda uwu kuti ndiuwononge.”
Amadziwikanso ndi dzina lakuti Yehoahazi.
Mʼchilankhulo choyambirira, “zowawa za pobereka.”
Amadziwikanso ndi dzina lakuti Yehoyakini ndi Yekoniya.
Mʼchilankhulo choyambirira, “Nebukadirezara.” Kameneka ndi kalembedwe kena ka dzinali.
Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼmasiku a moyo wake.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “pamene ndidzachititsa kuti mʼbanja la Davide mutuluke mbadwa yolungama.”
Kapena kuti, “onse ndi ampatuko.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Amalimbitsa manja a.”
Kapena kuti, “Iwo akukuchititsani kuti muziyembekezera zinthu zabodza.”
Kapena kuti, “uthenga wolemera.” Mawu ake a Chiheberi ali ndi matanthauzo awiri awa: “Uthenga wolemera wochokera kwa Mulungu” kapena “chinthu cholemera.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Nebukadirezara.” Kameneka ndi kalembedwe kena ka dzinali.
Amadziwikanso ndi dzina lakuti Yehoyakini ndi Koniya.
Mabaibulo ena amati, “anthu omanga makoma achitetezo.”
Kapena kuti, “matenda.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Nebukadirezara.” Kameneka ndi kalembedwe kena ka dzinali.
Mʼchilankhulo choyambirira, “ndakhala ndikudzuka mʼmawa nʼkumalankhula.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Ankadzuka mʼmawa nʼkuwatumiza.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Nebukadirezara.” Kameneka ndi kalembedwe kena ka dzinali.
Zikuoneka kuti limeneli ndi dzina lina la Babele (Babulo).
Kapena kuti, “wamanyenje.”
Kapena kuti, “kudzagwada.”
Kapena kuti, “potsatira malangizo anga amene.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “amene ndikudzuka mʼmawa nʼkuwatumiza.”
Kapena kuti, “Ndipo phiri pamene pali kachisi.”
Kapena kuti, “komanso kuyesa kufewetsa nkhope ya Yehova.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “amene ndikuona kuti ndi woyenerera.”
Kapena kuti, “matenda.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “upumule.”
Imeneyi ndi thanki yakopa yapakachisi.
Mʼchilankhulo choyambirira, “Ame!”
Kapena kuti, “matenda oti agwere.”
Mabaibulo ena amati, “komanso anthu omanga makoma achitetezo.”
Kapena kuti, “matenda.”
Mabaibulo ena amati, “zophulika.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “amene ndinkadzuka mʼmawa nʼkuwatumiza.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Nebukadirezara.” Kameneka ndi kalembedwe kena ka dzinali.
Kapena kuti, “mʼchiuno.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “lidzakhala lalikulu.”
Kapena kuti, “Ndidzakulangiza.”
Mabaibulo ena amati, “Ndidzawapatsa ulemerero.”
Kapena kuti, “Nʼchifukwa chake ndapitiriza kukusonyeza chikondi chokhulupirika.”
Kapena kuti, “kukavina pamodzi ndi anthu amene akuseka.”
Kapena kuti, “kumakhwawa a madzi.”
Kapena kuti, “chifukwa cha zinthu zabwino zochokera kwa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Ansembe ndidzawanenepetsa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Nʼchifukwa chake mʼmimba mwanga mwabwadamuka.”
Ena amati kuyayamira.
Mabaibulo ena amati, “mwamuna wawo.”
Kapena kuti, “phulusa lamafuta,” kutanthauza phulusa losakanikirana ndi mafuta a nsembe.
Mʼchilankhulo choyambirira, “Nebukadirezara.” Kameneka ndi kalembedwe kena ka dzinali.
Sekeli imodzi inali yofanana ndi magalamu 11.4. Onani Zakumapeto B14.
Mʼchilankhulo choyambirira, “mumabwezera pachifuwa cha ana.”
Kapena kuti, “matenda.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Nebukadirezara.” Kameneka ndi kalembedwe kena ka dzinali.
Mʼchilankhulo choyambirira, “Ngakhale kuti ndinkadzuka mʼmamawa nʼkumawaphunzitsa.”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena, “Gehena.”
Kapena kuti, “azidutsitsa.”
Kapena kuti, “Ndipo mʼmaganizo mwangamu simunabwerepo.”
Kapena kuti, “wolowa mʼmalo wolungama.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “kuchuluka kwa magulu ankhondo akumwamba.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu ya Abulahamu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Nebukadirezara.” Kameneka ndi kalembedwe kena ka dzinali.
Mʼchilankhulo choyambirira, “lero.”
Kapena kuti, “matenda.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Yonadabu,” chidule cha dzina lakuti Yehonadabu.
Mʼchilankhulo choyambirira, “Yonadabu,” chidule cha dzina lakuti Yehonadabu.
Mʼchilankhulo choyambirira, “Nebukadirezara.” Kameneka ndi kalembedwe kena ka dzinali.
Mʼchilankhulo choyambirira, “ndakhala ndikudzuka mʼmamawa nʼkumalankhula nanu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Ndinkadzuka mʼmamawa nʼkuwatumiza.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Yonadabu,” chidule cha dzina lakuti Yehonadabu.
Kapena kuti, “mlembi.”
Kapena kuti, “Nduna zonse za panyumba ya mfumu zinali zitakhala.”
Mweziwu unkayamba cha pakati pa November mpaka pakati pa December. Onani Zakumapeto B15.
Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu yake.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Nebukadirezara.” Kameneka ndi kalembedwe kena ka dzinali.
Mʼchilankhulo choyambirira, “anamuika mʼnyumba yamatangadza.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “anamuika mʼnyumba yachitsime.”
Kapena kuti, “matenda.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “amene adzapite.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mukapita kwa akalonga.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Koma ngati simudzapita kwa akalonga.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Koma mukakana kupita.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Amuna amene munkakhala nawo pa mtendere.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Nebukadirezara.” Kameneka ndi kalembedwe kena ka dzinali.
Kapena kuti, “Nerigali-sarezera, Samugari-nebo, Sarisekimu, Rabisarisi,” potengera kagawidwe kena ka mawu a Chiheberi.
Kapena kuti, “mkulu wa azamatsenga (wolosera zamʼtsogolo).”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Nebukadirezara.” Kameneka ndi kalembedwe kena ka dzinali.
Kapena kuti, “amkuwa.”
Mabaibulo ena amati, “azigwiramo ntchito yokakamiza.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Nebukadirezara.” Kameneka ndi kalembedwe kena ka dzinali.
Kapena kuti, “nduna yaikulu.”
Kapena kuti, “mkulu wa azamatsenga (wolosera zamʼtsogolo).”
Mʼchilankhulo choyambirira, “kuti ndiziima pamaso pa.”
Mawu akuti “zipatso zamʼchilimwe” akunena za nkhuyu ndipo nthawi zina amatanthauza zipatso za kanjedza.
Mʼchilankhulo choyambirira, “anali mbewu ya ufumu.”
Mabaibulo ena amati, “chidziwe chachikulu ku Gibiyoni.”
Kapena kuti, “nʼkukakhala kwa kanthawi.”
Kapena kuti, “matenda.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Nebukadirezara.” Kameneka ndi kalembedwe kena ka dzinali.
Kapena kuti, “Akachisi a milungu.”
Kapena kuti, “osavulazidwa.”
Kapena kuti, “Nyumba ya (Kachisi wa) Dzuwa,” kutanthauza Heliyopolisi.
Kapena kuti, “akachisi a milungu.”
Kapena kuti, “Memfisi.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Ine ndinkadzuka mʼmawa kwambiri nʼkutumiza.”
Kapena kuti, “Iwo sanadzimvere chisoni.”
Kapena kuti, “matenda.”
Limeneli ndi dzina laulemu la mulungu wamkazi amene Aisiraeli opanduka ankamulambira. Iwo ankakhulupirira kuti ameneyu ndi mulungu amene ankathandiza akazi kuti azibereka.
Limeneli ndi dzina laulemu la mulungu wamkazi amene Aisiraeli opanduka ankamulambira. Iwo ankakhulupirira kuti ameneyu ndi mulungu amene ankathandiza akazi kuti azibereka.
Limeneli ndi dzina laulemu la mulungu wamkazi amene Aisiraeli opanduka ankamulambira. Iwo ankakhulupirira kuti ameneyu ndi mulungu amene ankathandiza akazi kuti azibereka.
Limeneli ndi dzina laulemu la mulungu wamkazi amene Aisiraeli opanduka ankamulambira. Iwo ankakhulupirira kuti ameneyu ndi mulungu amene ankathandiza akazi kuti azibereka.
Mʼchilankhulo choyambirira, “Nebukadirezara.” Kameneka ndi kalembedwe kena ka dzinali.
Kapena kuti, “iwe ukuyembekezera.”
Kapena kuti, “iwe ndidzakulola kuti upulumutse moyo wako.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Nebukadirezara.” Kameneka ndi kalembedwe kena ka dzinali.
Mʼchilankhulo choyambirira, “Nebukadirezara.” Kameneka ndi kalembedwe kena ka dzinali.
Kapena kuti, “ku Memfisi.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “wataya nthawi imene anasankhiratu.”
Kutanthauza amene adzagonjetse Iguputo.
Kapena kuti, “Memfisi.”
Mabaibulo ena amati, “Udzasanduka bwinja.”
Kapena kuti, “amene akukatola nkhuni.”
Amene ndi Thebesi.
Mʼchilankhulo choyambirira, “Nebukadirezara.” Kameneka ndi kalembedwe kena ka dzinali.
Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”
Kapena kuti, “Ndidzakulangiza.”
Kutanthauza, “Kerete.”
Kapena kuti, “Malo okwezeka achitetezo.”
Mtengo wa junipa ndi wofanana ndi mtengo wa mkungudza.
Kapena kuti, “malo afulati apamwamba pa phiri.”
Mabaibulo ena amati, “pansi pouma.”
Kapena kuti, “chafika malo afulati apamwamba pa phiri.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Nyanga.”
Mawu akuti “zipatso zamʼchilimwe” makamaka amatanthauza nkhuyu ndipo nthawi zina amatanthauza zipatso za kanjedza.
Kapena kuti, “udzachitire phokoso.”
Chimenechi ndi chitoliro chimene ankaliza polira maliro.
Kapena kuti, “udzachitira phokoso.”
Chimenechi ndi chitoliro chimene ankaliza polira maliro.
Mabaibulo ena amati, “kumveke mfuwu ya nkhondo.”
Kapena kuti, “mʼmakola a nkhosa.”
Kapena kuti, “akufuna.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Nebukadirezara.” Kameneka ndi kalembedwe kena ka dzinali.
Mʼchilankhulo choyambirira, “Nebukadirezara.” Kameneka ndi kalembedwe kena ka dzinali.
Mʼchilankhulo choyambirira, “kumphepo zonse.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “umene ndi chiyambi cha mphamvu zawo.”
Mawu ake a Chiheberi amatanthauzanso “ndowe,” ndipo amagwiritsidwa ntchito ngati mawu onyoza.
Mawu akuti “kumemesa” amatanthauza zimene nyama yamphongo imachita ikafuna kukwera.
Mʼchilankhulo choyambirira, “wapereka dzanja lake.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Nebukadirezara.” Kameneka ndi kalembedwe kena ka dzinali.
Mʼchilankhulo choyambirira, “adzakhalitsidwa chete.”
Kapena kuti, “lidzawononga aneneri abodza.”
Mawu akuti “mwana wamkazi wa Babulo” ndi mawu a ndakatulo ndipo nthawi zambiri amanena za mzinda wa Babulo kapena anthu amene ankakhala mumzindawo.
Zikuoneka kuti akunena Ababulo.
Kapena kuti, “akufuna.”
Zikuoneka kuti limeneli ndi dzina lina la Kasidi.
Mabaibulo ena amati, “Dzazani tizikwama toikamo mivi.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “wadzutsa mitima ya.”
Kapena kuti, “nthunzi.”
Kapena kuti, “mpweya.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Yeretsani.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Yeretsani.”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mawu akuti “mwana wamkazi wa Babulo” ndi mawu a ndakatulo ndipo nthawi zambiri amanena za mzinda wa Babulo kapena anthu amene ankakhala mumzindawo.
Mʼchilankhulo choyambirira, “Nebukadirezara.” Kameneka ndi kalembedwe kena ka dzinali.
Kapena kuti, “mikango yaingʼono yamanyenje.”
Zikuoneka kuti limeneli ndi dzina lina la Babele (Babulo).
Kapena kuti, “anthu ochokera kudziko lina.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Nebukadirezara.” Kameneka ndi kalembedwe kena ka dzinali.
Kapena kuti, “amkuwa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Nebukadirezara.” Kameneka ndi kalembedwe kena ka dzinali.
Mʼchilankhulo choyambirira, “mikono 18.” Onani Zakumapeto B14.
Mʼchilankhulo choyambirira, “mikono 12.” Onani Zakumapeto B14.
Mʼchilankhulo choyambirira, “mphipi ya zala 4.” Onani Zakumapeto B14.
Mʼchilankhulo choyambirira, “mikono 5.” Onani Zakumapeto B14.
“Makangaza” ndi mtundu wa chipatso. Ena amati chimanga chachizungu.
Mʼchilankhulo choyambirira, “Nebukadirezara.” Kameneka ndi kalembedwe kena ka dzinali.
Mʼchilankhulo choyambirira, “Nebukadirezara.” Kameneka ndi kalembedwe kena ka dzinali.
Mʼchilankhulo choyambirira, “Nebukadirezara.” Kameneka ndi kalembedwe kena ka dzinali.
Mʼchilankhulo choyambirira, “anatukula mutu wa.”