Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • nwt Zechariah 1:1-14:21
  • Zekariya

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zekariya
  • Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Zekariya

ZEKARIYA

1 Mʼmwezi wa 8, mʼchaka chachiwiri cha ulamuliro wa Dariyo,+ Yehova analankhula ndi mneneri Zekariya*+ mwana wa Berekiya, mwana wa Ido, kuti: 2 “Yehova anakwiyira kwambiri makolo anu.+

3 Uwauze kuti, ‘Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti: “Bwererani kwa ine,” watero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, “ndipo ine ndidzabwerera kwa inu,”+ akutero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.’”

4 “‘Musakhale ngati makolo anu amene aneneri akale anawauza kuti: “Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti, ‘Chonde, siyani njira zanu zoipa ndiponso zochita zanu zoipa.’”’+

‘Koma iwo sanamvere ndipo sanatsatire mawu anga,’+ watero Yehova.

5 ‘Kodi makolo anuwo ali kuti pano? Ndipo “kodi aneneriwo anakhalabe ndi moyo mpaka kalekale?” 6 Ndinauza makolo anu malamulo oti azitsatira ndipo ndinatumiza atumiki anga aneneri kuti akawachenjeze zimene zidzawachitikire ngati sangatsatire malamulowo. Kodi zonse zimene ndinanena kuti zidzawachitikirazo sizinawachitikire?’+ Choncho iwo anabwerera kwa ine nʼkunena kuti: ‘Yehova wa magulu ankhondo akumwamba watichitira zimene anakonza mogwirizana ndi njira zathu ndi zochita zathu.’”+

7 Pa tsiku la 24 la mwezi wa 11 womwe ndi mwezi wa Sebati,* mʼchaka chachiwiri cha ulamuliro wa Dariyo,+ Yehova analankhula ndi mneneri Zekariya mwana wa Berekiya, mwana wa Ido. Anamuuza kuti anene kuti: 8 “Ndinaona masomphenya usiku. Ndinaona munthu atakwera pahatchi* yomwe inaima pakati pa mitengo ya mchisu imene inali mʼchigwa. Kumbuyo kwake kunali mahatchi ofiira kwambiri, ofiirira ndi oyera.”*

9 Choncho ndinafunsa kuti: “Kodi amenewa ndi ndani mbuyanga?”

Mngelo amene ankalankhula nane anandiyankha kuti: “Ndikuuza kuti amenewa ndi ndani.”

10 Kenako munthu amene anaima pakati pa mitengo ya mchisu uja anati: “Amenewa atumizidwa ndi Yehova kuti ayendeyende padziko lapansi.” 11 Ndiyeno iwo anauza mngelo wa Yehova amene anaima pakati pa mitengo ya mchisu uja kuti: “Ife tayendayenda padziko lonse lapansi ndipo taona kuti pali bata komanso palibe chosokoneza.”+

12 Choncho mngelo wa Yehova anati: “Inu Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, kodi Yerusalemu ndiponso mizinda ya Yuda+ imene munaikwiyira kwa zaka 70 zimenezi,+ simuichitira chifundo mpaka liti?”

13 Yehova anayankha mngelo amene ankalankhula nane uja mokoma mtima komanso ndi mawu olimbikitsa. 14 Ndiyeno mngelo amene ankalankhula nane uja anandiuza kuti: “Fuula kuti, ‘Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti: “Ndatsimikiza mtima kuti nditeteze Yerusalemu ndi Ziyoni.+ 15 Ndakwiyira kwambiri anthu a mitundu ina amene akukhala mosatekeseka.+ Ndawakwiyira chifukwa chakuti ine ndinangokwiyira anthu anga pangʼono,+ koma anthu amenewa anakulitsa kwambiri mavuto a anthu angawo.”’+

16 Choncho Yehova wanena kuti, ‘“Ndidzabwerera ku Yerusalemu nʼkuchitira chifundo mzinda umenewu+ ndipo nyumba yanga idzamangidwa mumzindawu.+ Chingwe choyezera chidzatambasulidwa pa Yerusalemu,”+ watero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.’

17 Fuulanso kuti, ‘Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti: “Mizinda yanga idzasefukiranso ndi zinthu zabwino. Yehova adzalimbikitsanso Ziyoni+ ndipo adzasankhanso Yerusalemu.”’”+

18 Kenako nditakweza maso, ndinaona nyanga 4.+ 19 Choncho ndinafunsa mngelo amene ankalankhula nane uja kuti: “Kodi nyangazi zikuimira chiyani?” Iye anandiyankha kuti: “Izi ndi nyanga zimene zinabalalitsa Yuda,+ Isiraeli+ ndi Yerusalemu.”+

20 Kenako Yehova anandionetsa amisiri 4. 21 Ndiyeno ndinafunsa kuti: “Kodi awa abwera kudzatani?”

Mngeloyo anayankha kuti: “Zimenezi ndi nyanga zimene zinabalalitsa Yuda moti panalibe amene anatha kudzutsa mutu wake. Amisiriwa adzabwera kudzaopseza nyangazi ndipo adzawononga nyanga za mitundu ina ya anthu amene anakweza nyanga* zawo poukira dziko la Yuda kuti abalalitse anthu ake.”

2 Kenako ndinakweza maso ndipo ndinaona munthu atanyamula chingwe choyezera.+ 2 Ndiyeno ndinamʼfunsa kuti: “Ukupita kuti?”

Iye anandiyankha kuti: “Ndikupita kukayeza Yerusalemu kuti ndidziwe kutalika kwa mulitali ndi mulifupi mwake.”+

3 Kenako mngelo amene ankalankhula ndi ine uja ananyamuka nʼkumapita ndipo kunabwera mngelo wina kudzakumana naye. 4 Mngeloyo anauza mnzakeyo kuti: “Thamanga ukauze mnyamata uyo kuti, ‘“Mu Yerusalemu anthu azidzakhalamo+ ngati mzinda wopanda mpanda chifukwa cha anthu onse ndiponso ziweto zimene zili mmenemo.+ 5 Ine ndidzakhala ngati mpanda wake wamoto+ ndipo ulemerero wanga udzadzaza mumzindawu,”’+ watero Yehova.”

6 “Bwerani! Bwerani! Thawani mʼdziko lakumpoto,”+ watero Yehova.

“Chifukwa ndinakubalalitsirani kumbali zonse za dziko lapansi,”+ watero Yehova.

7 “Bwera Ziyoni! Thawa iwe amene ukukhala ndi mwana wamkazi wa Babulo.*+ 8 Atapatsidwa ulemerero, Mulungu wandituma kwa anthu a mitundu ina amene ankakulandani zinthu zanu,+ chifukwa Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti, ‘Amene akukukhudzani, akukhudza mwana wa diso langa.+ 9 Ine ndidzawaloza mowaopseza, ndipo adzatengedwa ndi akapolo awo kuti akhale chuma cha akapolowo.’+ Mudzadziwa ndithu kuti Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wandituma.

10 Fuula chifukwa cha chisangalalo, iwe mwana wamkazi wa Ziyoni,*+ popeza ine ndikubwera+ ndipo ndidzakhala pakati pako,”+ watero Yehova. 11 “Pa tsiku limenelo mitundu yambiri ya anthu idzakhala kumbali ya Yehova+ ndipo adzakhala anthu anga. Ine ndidzakhala pakati pako.” Ndipo udzadziwa kuti Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wandituma kwa iwe. 12 Yehova adzatenga Yuda kukhala gawo lake mʼdziko loyera, ndipo adzasankhanso Yerusalemu.+ 13 Anthu nonsenu, khalani chete pamaso pa Yehova, chifukwa iye wanyamuka pamalo ake oyera okhala ndipo akufuna kuchitapo kanthu.

3 Ndiyeno Mulungu anandionetsa Yoswa+ mkulu wa ansembe, ataimirira pamaso pa mngelo wa Yehova. Satana+ anali ataima kudzanja lamanja la Yoswa kuti azimutsutsa. 2 Kenako mngelo wa Yehovayo anauza Satana kuti: “Iwe Satana, Yehova akudzudzule!+ Yehova amene wasankha Yerusalemu+ akudzudzule. Kodi munthu uyu sali ngati chikuni chimene chapulumutsidwa pamoto kuti chisapse?”

3 Pa nthawiyi, Yoswa anali ataima pamaso pa mngelo, atavala zovala zonyansa. 4 Mngeloyo anauza anthu amene anaima patsogolo pake kuti: “Muvuleni zovala zonyansazo.” Kenako anauza Yoswa kuti: “Waona, ndakuchotsera zolakwa zako ndipo uvekedwa zovala zabwino kwambiri.”*+

5 Choncho ndinanena kuti: “Auzeni kuti amuveke nduwira yoyera kumutu kwake.”+ Ndipo anamuvekadi nduwira yoyera kumutu kwake komanso zovala zina. Apa nʼkuti mngelo wa Yehova ataima chapafupi. 6 Mngelo wa Yehova uja anauza Yoswa kuti: 7 “Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti, ‘Ukayenda mʼnjira zanga ndi kutsatira malamulo anga, udzakhala woweruza wa anthu a mʼnyumba yanga+ ndipo uzidzasamalira* mabwalo a nyumba yanga. Komanso ndidzakulola kumafika pamaso panga ngati mmene amachitira aima apawa.’

8 ‘Tamvetsera iwe Yoswa mkulu wa ansembe ndi anzako amene akhala pansi kutsogolo kwako, chifukwa amuna amenewa ali ngati chizindikiro. Ine ndibweretsa mtumiki wanga+ dzina lake Mphukira.+ 9 Taonani mwala umene ndauika pamaso pa Yoswa. Mwala umenewu uli ndi maso 7 ndipo pamwalawu ndilembapo zinthu mochita kugoba. Ndidzachotsa zolakwa za dzikoli tsiku limodzi,’+ watero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.

10 ‘Pa tsiku limenelo aliyense adzaitana mnzake kuti abwere pansi pa mtengo wake wa mpesa ndiponso wa mkuyu,’+ watero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.”

4 Mngelo amene ankalankhula ndi ine uja anabwerera nʼkundidzutsa ngati akudzutsa munthu amene akugona. 2 Kenako anandifunsa kuti: “Ukuona chiyani?”

Ndinayankha kuti: “Ndikuona choikapo nyale chagolide yekhayekha.+ Pamwamba pake pali mbale yolowa. Choikapo nyalecho chili ndi nyale 7,+ inde nyale 7, ndipo nyale zimene zili pachoikapo nyalecho, zilinso ndi mapaipi 7. 3 Pafupi ndi choikapo nyalecho pali mitengo iwiri ya maolivi.+ Umodzi uli kumanja kwa mbale yolowa ija ndipo wina uli kumanzere kwa mbaleyo.”

4 Kenako ndinafunsa mngelo amene ankalankhula nane uja kuti: “Kodi zimenezi zikuimira chiyani mbuyanga?” 5 Mngeloyo anafunsa kuti: “Kodi sukudziwa tanthauzo la zinthu zimenezi?”

Ndinayankha kuti: “Sindikudziwa mbuyanga.”

6 Choncho iye anandiuza kuti: “Yehova wauza Zerubabele kuti, ‘“Kuti zinthu zonsezi zichitike, sipakufunika gulu lankhondo kapena mphamvu,+ koma mzimu wanga,”+ watero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba. 7 Ngakhale Zerubabele+ atakumana ndi chopinga chachikulu ngati phiri, chidzasalazidwa nʼkukhala malo afulati.+ Iye adzabweretsa mwala wotsiriza ndipo anthu adzafuula kuti: “Koma mwalawu ndiye ndi wokongola bwanji! Koma ndiye ndi wokongola!”’”

8 Ndinamvanso mawu a Yehova akuti: 9 “Manja a Zerubabele anayala maziko a nyumbayi+ ndipo manja ake omwewo adzaimalizitsa.+ Ndipo mudzadziwa kuti Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wandituma kwa inu. 10 Munthu asakunyozeni chifukwa chakuti munayamba kumanga ndi zinthu zochepa.+ Popeza anthu adzasangalala ndipo adzaona chingwe choyezera cha mmisiri womanga, mʼdzanja la Zerubabele. Nyale 7 zimenezi* ndi maso a Yehova amene akuyangʼana uku ndi uku padziko lonse lapansi.”+

11 Ndiyeno ndinafunsa mngelo uja kuti: “Kodi mitengo iwiri ya maolivi, imene wina uli kumanja ndipo wina kumanzere kwa choikapo nyalechi, ikuimira chiyani?”+ 12 Ndinamufunsanso kuti: “Kodi nthambi* ziwiri za mitengo ya maolivi, zimene zikuthira mafuta agolide mʼmbale yolowa kudzera mʼmapaipi awiri agolide, zikuimira chiyani?”

13 Iye anandifunsa kuti: “Kodi sukudziwa tanthauzo la zinthu zimenezi?”

Ndinayankha kuti: “Ayi mbuyanga.”

14 Ndiyeno iye anandiuza kuti: “Amenewa ndi odzozedwa awiri amene amaima kumbali iyi ndi mbali inayi ya Ambuye wa dziko lonse lapansi.”+

5 Nditayangʼananso kumwamba, ndinaona mpukutu ukuuluka. 2 Mngeloyo anandifunsa kuti: “Ukuona chiyani?”

Ndinayankha kuti: “Ndikuona mpukutu ukuuluka. Mpukutuwo ndi wautali mikono* 20 mulitali ndiponso mikono 10 mulifupi.”

3 Ndiyeno anandiuza kuti: “Ili ndi temberero limene likubwera padziko lonse lapansi, chifukwa aliyense amene akuba,+ mogwirizana ndi zimene zalembedwa kumbali imodzi ya mpukutuwo, sakulandira chilango. Komanso aliyense amene akulumbira mwachinyengo,+ mogwirizana ndi zimene zalembedwa kumbali ina ya mpukutuwo, sakulandira chilango. 4 Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti, ‘Ine ndatumiza mpukutuwo kuti ukalowe mʼnyumba ya munthu wakuba ndi mʼnyumba ya munthu wolumbira mwachinyengo mʼdzina langa. Mpukutuwo udzakhalabe mʼnyumba mwake nʼkuwonongeratu nyumbayo, matabwa ake ndi miyala yake.’”

5 Kenako mngelo amene ankalankhula nane uja anandiyandikira nʼkundiuza kuti: “Taona chimene chikubwera uko.”

6 Choncho ndinafunsa kuti: “Nʼchiyani chimenechi?”

Iye anandiyankha kuti: “Chimenechi ndi chiwiya chokwana muyezo wa efa.”* Ndiyeno anapitiriza kuti: “Anthu oipa amaoneka chonchi padziko lonse lapansi.” 7 Kenako ndinaona akuvundukula chivundikiro chamtovu cha chiwiyacho, ndipo mkati mwake munali mzimayi atakhala pansi. 8 Mngelo uja anandiuza kuti: “Mayi ameneyu dzina lake ndi Kuipa.” Kenako anamukankha nʼkumubwezera mʼchiwiya chokwana muyezo wa efacho ndipo anachivundikira ndi chivundikiro chamtovu chija.

9 Ndiyeno nditayangʼana kumwamba ndinaona azimayi awiri akubwera. Azimayiwo ankauluka mphepo ikuwomba ndipo mapiko awo anali ooneka ngati a dokowe. Iwo ananyamula chiwiya chija nʼkupita nacho mʼmwamba.* 10 Choncho ndinafunsa mngelo amene ankalankhula nane uja kuti: “Kodi chiwiyacho akupita nacho kuti?”

11 Iye anandiyankha kuti: “Akupita nacho kudziko la Sinara*+ kuti akamangire mzimayiyo nyumba kumeneko. Akakamumangira nyumbayo, akamukhazika kumeneko pamalo ake oyenera.”

6 Kenako nditayangʼananso kumwamba ndinaona magaleta 4 akubwera kuchokera pakati pa mapiri awiri. Mapiriwo anali akopa.* 2 Galeta loyamba linkakokedwa ndi mahatchi ofiira ndipo galeta lachiwiri linkakokedwa ndi mahatchi akuda.+ 3 Galeta lachitatu linkakokedwa ndi mahatchi oyera ndipo galeta la 4 linkakokedwa ndi mahatchi amawangamawanga ndiponso amadonthomadontho.+

4 Ndiyeno ndinafunsa mngelo amene ankalankhula nane uja kuti: “Kodi magaleta amenewa akuimira chiyani mbuyanga?”

5 Mngeloyo anandiyankha kuti: “Magaletawa akuimira zolengedwa zauzimu 4+ zakumwamba zomwe zinakaima pamaso pa Ambuye wa dziko lonse lapansi+ ndipo zikubwera. 6 Galeta limene likukokedwa ndi mahatchi akuda likupita kudziko lakumpoto.+ Mahatchi oyera akupita kutsidya la nyanja. Mahatchi amawangamawanga akupita kudziko lakumʼmwera. 7 Mahatchi amadonthomadontho anali okonzeka kupita nʼkumakayendayenda padziko lapansi.” Kenako iye anauza mahatchiwo kuti: “Pitani mukayendeyende padziko lapansi.” Ndipo mahatchiwo anapita nʼkumakayendayenda padziko lapansi.

8 Mngelo uja anandiitana nʼkundiuza kuti: “Taona, mkwiyo umene Yehova anali nawo padziko lakumpoto watha chifukwa cha mahatchi amene apita kumeneko.”

9 Yehova analankhula nanenso kuti: 10 “Ukatenge kwa Heledai, Tobiya ndi Yedaya zinthu zimene abweretsa kuchokera kwa anthu amene anatengedwa kupita ku ukapolo. Pa tsiku limenelo udzapite kunyumba ya Yosiya mwana wa Zefaniya pamodzi ndi anthu amene achokera ku Babulowo. 11 Ukatenge siliva ndi golide nʼkupangira chisoti chachifumu.* Chisoticho udzaveke Yoswa+ mkulu wa ansembe, mwana wa Yehozadaki. 12 Ndiyeno udzamuuze kuti,

‘Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti: “Munthu uyu dzina lake ndi Mphukira.+ Adzaphuka pamalo ake ndipo adzamanga kachisi wa Yehova.+ 13 Munthu ameneyu ndi amene adzamange kachisi wa Yehova ndipo adzalandira ulemerero. Iye adzakhala pampando wake wachifumu nʼkumalamulira. Adzakhalanso wansembe ali pampando womwewo+ ndipo maudindo awiri onsewo adzakhala ogwirizana. 14 Chisoti chachifumucho* chizidzakhala mʼkachisi wa Yehova kuti anthu azidzakumbukira Helemu, Tobiya, Yedaya+ ndi Heni mwana wa Zefaniya. 15 Anthu amene ali kutali adzabwera kudzamanga nawo kachisi wa Yehova.” Anthu inu mukadzamvera mawu a Yehova Mulungu wanu, mudzadziwa kuti Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wandituma kwa inu.’”

7 Mʼchaka cha 4 cha ulamuliro wa Mfumu Dariyo, Yehova analankhula ndi Zekariya+ pa tsiku la 4 la mwezi wa 9, womwe ndi mwezi wa Kisilevi.* 2 Anthu a ku Beteli anatumiza Sarezere komanso Regemu-meleki ndi anthu ake, kuti akapemphe Yehova kuti awakomere mtima.* 3 Anawatuma kuti akauze ansembe apanyumba* ya Yehova wa magulu ankhondo akumwamba ndi aneneri kuti: “Kodi tilire* mʼmwezi wa 5+ ndiponso kusala kudya ngati mmene tachitira zaka zonsezi?”

4 Yehova wa magulu ankhondo akumwamba analankhula nanenso kuti: 5 “Kauze anthu onse amʼdzikoli ndi ansembe kuti, ‘Pamene munkasala kudya ndi kulira mʼmwezi wa 5 komanso mʼmwezi wa 7+ kwa zaka 70,+ kodi munkasaladi kudya chifukwa cha ine? 6 Ndipo pamene munkadya komanso kumwa, kodi simunkachita zimenezi kuti mudzisangalatse nokha? 7 Kodi simunayenera kumvera mawu amene Yehova ananena kudzera mwa aneneri akale,+ pamene ku Yerusalemu ndi mizinda yozungulira kunkakhala anthu komanso kunali mtendere? Kodi simunayenera kumvera Mulungu pamene ku Negebu ndi ku Sefela kunkakhala anthu?’”

8 Yehova analankhulanso ndi Zekariya kuti: 9 “Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti, ‘Muziweruza mwachilungamo chenicheni+ komanso muzisonyezana chikondi chokhulupirika+ ndi chifundo. 10 Musamabere mwachinyengo mkazi wamasiye, mwana wamasiye,*+ mlendo+ kapena munthu wosauka.+ Musamakonzerane chiwembu mumtima mwanu.’+ 11 Koma iwo anakanabe kumvetsera.+ Anapitiriza kumulozetsa nkhongo+ ndipo anatseka makutu awo kuti asamve.+ 12 Iwo anaumitsa mtima wawo ngati mwala wa dayamondi*+ ndipo sanamvere malamulo* ndi mawu a Yehova wa magulu ankhondo akumwamba amene anawatumizira pogwiritsa ntchito mzimu wake kudzera mwa aneneri akale.+ Choncho Yehova wa magulu ankhondo akumwamba anakwiya kwambiri.”+

13 “‘Ine ndikawaitana sankandimvera,+ choncho iwonso akandiitana sindinkawamvera,’+ watero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba. 14 ‘Ndipo ndinawabalalitsira ku mitundu yonse ya anthu imene sankaidziwa+ ngati atengedwa ndi mphepo yamkuntho. Dzikoli analisiya ndipo linakhala bwinja, popanda munthu wodutsamo kapena kubwereramo.+ Chifukwa anasandutsa dziko losiririka kukhala chinthu chochititsa mantha.’”

8 Yehova wa magulu ankhondo akumwamba analankhula nanenso kuti: 2 “Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti: ‘Ndatsimikiza mtima kuti ndidzateteza Ziyoni.+ Ndatsimikiza kuti ndidzamuteteza nditakwiya kwambiri.’”

3 “Yehova wanena kuti, ‘Ndidzabwerera ku Ziyoni+ ndipo ndizidzakhala ku Yerusalemu.+ Yerusalemu adzatchedwa mzinda wa choonadi*+ ndipo phiri la Yehova wa magulu ankhondo akumwamba lidzatchedwa phiri loyera.’”+

4 “Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti, ‘Amuna ndi akazi achikulire adzakhalanso mʼmabwalo a mzinda wa Yerusalemu, aliyense atanyamula ndodo mʼmanja mwake chifukwa cha ukalamba.*+ 5 Mʼmabwalo a mzindawo mudzadzaza anyamata ndi atsikana ndipo azidzasewera mmenemo.’”+

6 “Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti, ‘Ngakhale kuti pa nthawiyo anthu omwe adzatsale adzaona kuti zimenezo nʼzosatheka, kodi zidzakhalanso zosatheka kwa ine?’ watero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.”

7 “Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti, ‘Ine ndipulumutsa anthu anga kuchokera kudziko lakumʼmawa ndiponso lakumadzulo.+ 8 Ndidzawabweretsa, ndipo azidzakhala mu Yerusalemu.+ Iwo adzakhala anthu anga ndipo ine ndidzakhala Mulungu wawo+ woona* ndi wachilungamo.’”

9 “Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti, ‘Limbani mtima ndipo mukonzeke kugwira ntchito,+ inu amene mukumva mawu a aneneri+ masiku ano. Awa ndi mawu amene ananenedwanso tsiku limene maziko a nyumba ya Yehova wa magulu ankhondo akumwamba anayalidwa kuti kachisi amangidwe. 10 Nthawi imeneyi isanafike, palibe malipiro omwe ankaperekedwa polipira munthu kapena chiweto.+ Zinali zoopsa kuyenda ulendo chifukwa cha adani, popeza ine ndinkachititsa kuti anthu onse aziukirana.’

11 ‘Koma tsopano anthu anga otsala sindidzawachitiranso zinthu ngati mmene ndinachitira masiku akale,’+ watero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba. 12 ‘Mʼdzikolo mudzadzalidwa mbewu ya mtendere. Mpesa udzabala zipatso ndipo dziko lapansi lidzatulutsa zokolola zake.+ Kumwamba kudzagwetsa mame ndipo ndidzachititsa kuti anthu otsala alandire zinthu zonsezi.+ 13 Popeza munali temberero pakati pa anthu a mitundu ina,+ inu a mʼnyumba ya Yuda ndi a mʼnyumba ya Isiraeli ndidzakupulumutsani ndipo mudzakhala dalitso.+ Limbani mtima,+ musachite mantha.’+

14 Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti, ‘“Monga zinalili kuti ndinatsimikiza mtima kukugwetserani tsoka chifukwa choti makolo anu anandikwiyitsa ndipo sindinakumvereni chisoni,”+ watero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, 15 “panopa ndatsimikizanso mtima kuchitira zabwino Yerusalemu ndi nyumba ya Yuda.+ Choncho musachite mantha.”’+

16 ‘Muzichita zinthu izi: Muziuzana zoona.+ Poweruza milandu mʼmageti a mizinda yanu, muziweruza mogwirizana ndi choonadi komanso molimbikitsa mtendere.+ 17 Musamakonzerane chiwembu mumtima mwanu+ ndipo musamakonde kulumbira monama.+ Chifukwa zinthu zonsezi ndimadana nazo,’+ watero Yehova.”

18 Yehova wa magulu ankhondo akumwamba analankhula nanenso kuti: 19 “Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti, ‘Kusala kudya kwa mʼmwezi wa 4,+ kusala kudya kwa mʼmwezi wa 5,+ kusala kudya kwa mʼmwezi wa 7+ ndiponso kusala kudya kwa mʼmwezi wa 10,+ idzakhala nthawi yachikondwerero komanso yosangalala kwa anthu a mʼnyumba ya Yuda.+ Choncho muzikonda choonadi ndiponso mtendere.’

20 Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti, ‘Ndithu anthu a mitundu ina ndi anthu amʼmizinda yambiri adzabwera. 21 Ndipo anthu amumzinda wina adzapita kwa anthu amumzinda wina nʼkuwauza kuti: “Tiyeni tipite tikapemphe Yehova kuti atikomere mtima* komanso tikafunefune Yehova wa magulu ankhondo akumwamba. Inenso ndipita nawo.”+ 22 Anthu ambiri a mitundu ina ndiponso mitundu yamphamvu idzabwera kudzafunafuna Yehova wa magulu ankhondo akumwamba mu Yerusalemu,+ ndiponso kudzapempha Yehova kuti awakomere mtima.’*

23 Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti, ‘Mʼmasiku amenewo, amuna 10 ochokera mʼzilankhulo zonse za anthu a mitundu ina+ adzagwira mkanjo* wa Myuda nʼkunena kuti: “Anthu inu tikufuna tipite nanu limodzi,+ chifukwa tamva kuti Mulungu ali ndi inu.”’”+

9 Uthenga wokhudza dziko la Hadiraki:

“Uwu ndi uthenga wa Yehova wokhudza dziko la Hadiraki,

Ndipo makamaka ukupita kumzinda wa Damasiko.+

Chifukwa maso a Yehova ali pa anthu,+

Komanso pa mafuko onse a Isiraeli.

 2 Uthengawu ukupitanso kwa Hamati+ amene anachita naye malire.

Komanso kwa Turo+ ndi Sidoni+ chifukwa ali ndi nzeru zambiri.+

 3 Turo anamanga malo okwera omenyerapo nkhondo.

Anadziunjikira siliva wambiri ngati fumbi,

Ndiponso golide wambiri ngati dothi lamʼmisewu.+

 4 Yehova adzamulanda zinthu zake.

Gulu lake lankhondo adzaliponyera mʼnyanja.+

Ndipo iye adzatenthedwa ndi moto.+

 5 Asikeloni adzaona zimenezi ndipo adzachita mantha.

Gaza adzamva ululu waukulu.

Izi zidzachitikiranso Ekironi chifukwa amene ankamudalira wachititsidwa manyazi.

Ku Gaza sikudzakhalanso mfumu,

Ndipo ku Asikeloni sikudzakhalanso anthu.+

 6 Mwana wochokera mu mtundu wina wa anthu azidzakhala ku Asidodi,

Ndipo ndidzathetsa kunyada kwa Afilisiti.+

 7 Ndidzachotsa zinthu zamagazi mʼkamwa mwawo,

Komanso chakudya chonyansa pakati pa mano awo.

Ndipo aliyense amene adzatsale, adzakhala wa Mulungu wathu.

Iye adzakhala ngati mtsogoleri mu Yuda,+

Ndipo Ekironi adzakhala ngati munthu wa Chiyebusi.+

 8 Ndidzamanga msasa kunja kwa nyumba yanga kuti ndizidzailondera,+

Moti sipadzakhala munthu wolowa kapena kutuluka.

Aliyense amene ankawagwiritsa ntchito* sadzadutsanso pakati pawo+

Chifukwa ine ndaona ndi maso anga.*

 9 Iwe mwana wamkazi wa Ziyoni* sangalala kwambiri.

Fuula mokondwera iwe mwana wamkazi wa Yerusalemu.*

Taona, mfumu yako ikubwera kwa iwe.+

Mfumuyo ndi yolungama ndipo ikubweretsa chipulumutso.*

Ndi yodzichepetsa+ ndipo ikubwera itakwera bulu.

Ikubwera itakwera mwana wamphongo wa bulu.+

10 Ndidzachotsa magaleta ankhondo ku Efuraimu

Ndiponso mahatchi ku Yerusalemu.

Mauta omenyera nkhondo adzachotsedwa.

Mfumuyo idzalalikira uthenga wamtendere kwa anthu a mitundu ina.+

Ulamuliro wake udzayambira kunyanja mpaka kukafika kunyanja ina.

Ndiponso kuchokera ku Mtsinje* mpaka kumalekezero a dziko lapansi.+

11 Koma mkazi iwe, chifukwa cha magazi a pangano limene unapangana ndi ine,

Ndidzatulutsa akaidi ako mʼdzenje lopanda madzi.+

12 Inu akaidi amene muli ndi chiyembekezo, bwererani kumalo a chitetezo champhamvu.+

Lero ndikukuuza kuti,

‘Mkazi iwe, ndidzakupatsa magawo awiri a madalitso.+

13 Ndidzapinda Yuda kuti akhale uta wanga.

Efuraimu ndidzamuika pa uta umenewo ngati muvi.

Ndidzadzutsa ana ako, iwe Ziyoni,

Kuti aukire ana a Girisi.

Ndipo ndidzakusandutsa lupanga la msilikali.’

14 Zidzakhala zoonekeratu kuti Yehova ali ndi anthu ake,

Ndipo muvi wake udzathamanga ngati mphezi.

Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa adzaliza lipenga,+

Ndipo adzapita ndi mphepo yamkuntho yakumʼmwera.

15 Yehova wa magulu ankhondo akumwamba adzateteza anthu ake.

Adani awo adzawaponyera miyala ndi gulaye,* koma iwo adzawagonjetsa.+

Iwo adzasangalala ndipo adzafuula ngati amwa vinyo.

Adzakhala ngati mbale zolowa zodzaza vinyo,

Ndiponso ngati magazi amene athiridwa mʼmakona a guwa lansembe.+

16 Pa tsiku limenelo, Yehova Mulungu adzapulumutsa nkhosa zake,

Zomwe ndi anthu ake.+

Popeza iwo adzakhala ngati miyala yamtengo wapatali yapachisoti chachifumu yomwe ikunyezimira mʼdziko lake.+

17 Ubwino wake ndi waukulu kwambiri,+

Ndiponso iye ndi wooneka bwino kwambiri.

Tirigu adzapatsa mphamvu anyamata,

Ndipo vinyo watsopano adzapatsa mphamvu anamwali.”+

10 “Pemphani Yehova kuti akugwetsereni mvula pa nthawi ya mvula yomalizira.

Yehova ndi amene amapanga mitambo yamvula,

Ndiponso amene amagwetsera anthu mvula.+

Iye amakulitsa mbewu mʼmunda mwa munthu aliyense.

 2 Aterafi* amalankhula zabodza,

Ndipo olosera zamʼtsogolo amaona masomphenya onama.

Amafotokoza maloto opanda pake,

Ndipo saphula kanthu polimbikitsa anthu.

Nʼchifukwa chake adzasochere ngati nkhosa.

Iwo adzavutika chifukwa adzakhala opanda mʼbusa.

 3 Ine ndakwiyira kwambiri abusa,

Ndipo atsogoleri awo opondereza* ndiwaimba mlandu.

Chifukwa ine Yehova wa magulu ankhondo akumwamba ndacheukira gulu langa la nkhosa+ lomwe ndi nyumba ya Yuda

Ndipo ndalisandutsa hatchi yanga yaulemerero, yokwera popita kunkhondo.

 4 Mʼnyumba ya Yuda mudzatuluka mtsogoleri.

Mudzatulukanso wolamulira wothandiza,

Komanso mudzatuluka uta womenyera nkhondo.

Woyangʼanira* aliyense adzatuluka mwa iye. Onse adzatulukira limodzi.

 5 Onsewa adzakhala ngati asilikali.

Adzapondaponda matope a mʼmisewu ya kunkhondo.

Iwo adzamenya nkhondo chifukwa Yehova ali nawo.+

Adani awo oyenda pamahatchi adzachitsidwa manyazi.+

 6 Ndidzachititsa nyumba ya Yuda kukhala yapamwamba,

Ndipo nyumba ya Yosefe ndidzaipulumutsa.+

Ndidzawabwezera pamalo awo amene ankakhala,

Chifukwa ndidzawachitira chifundo.+

Iwo adzakhala ngati sanakanidwepo chiyambire.+

Popeza ine ndine Yehova Mulungu wawo, ndidzawayankha.

 7 A nyumba ya Efuraimu adzakhala ngati msilikali wamphamvu,

Ndipo mumtima mwawo adzasangalala ngati amwa vinyo.+

Ana awo aamuna adzaona zimenezi ndipo adzakondwera.

Mitima yawo idzakondwera chifukwa cha Yehova.+

 8 ‘Ndidzawaitana ndi likhweru nʼkuwasonkhanitsa pamodzi.

Popeza ndidzawawombola,+ iwo adzachuluka.

Ndipo adzapitiriza kuchuluka.

 9 Ngakhale kuti ndidzawamwaza ngati mbewu pakati pa anthu a mitundu ina,

Iwo adzandikumbukira ali kumadera akutali.

Iwowo ndi ana awo adzapezanso mphamvu ndipo adzabwerera.

10 Ndidzawabweretsa kuchokera kudziko la Iguputo.

Ndidzawasonkhanitsa pamodzi kuchokera kudziko la Asuri.+

Ndidzawabweretsa kudera la Giliyadi+ ndi la Lebanoni

Ndipo malo okwanira anthu onsewo sadzapezeka.+

11 Ndidzadutsa panyanja, nyanjayo nditaigwetsera tsoka.

Ndidzamenya mafunde a nyanjayo,+

Ndipo madzi onse a mtsinje wa Nailo adzauma.

Kunyada kwa Asuri kudzathetsedwa,

Ndipo ndodo yachifumu ya Iguputo idzachoka.+

12 Ine Yehova ndidzawachititsa kukhala amphamvu,+

Ndipo zochita zawo zidzalemekeza dzina langa,’+ watero Yehova.”

11 “Iwe Lebanoni, tsegula zitseko zako,

Kuti moto uwotcheretu mitengo yako ya mkungudza.

 2 Lira mofuula, iwe mtengo wa junipa,* chifukwa mtengo wa mkungudza wagwa.

Mitengo ikuluikulu yawonongedwa.

Lirani mofuula, inu mitengo ya thundu* ya ku Basana,

Chifukwa nkhalango yowirira kwambiri ija yawonongedwa.

 3 Tamverani! Abusa akulira mofuula,

Chifukwa ulemerero wawo watha.

Tamverani! Mikango yamphamvu ikubangula,

Chifukwa nkhalango zowirira za mʼmbali mwa mtsinje wa Yorodano zawonongedwa.

4 Yehova Mulungu wanga wanena kuti, ‘Weta nkhosa zimene zinayenera kuphedwa.+ 5 Amene anazigula amazipha,+ koma saimbidwa mlandu. Amene akuzigulitsa+ akunena kuti: “Yehova atamandike chifukwa ndilemera.” Ndipo abusa ake sazichitira chifundo.’+

6 ‘Sindidzachitiranso chifundo anthu okhala mʼdzikoli,’ watero Yehova. ‘Choncho ine ndidzachititsa kuti aliyense aziponderezedwa ndi mnzake ndiponso mfumu yake. Iwo adzawononga dzikoli, ndipo ine sindidzawapulumutsa mʼmanja mwawo.’”

7 Ine ndinayamba kuweta nkhosa zimene zinayenera kuphedwa+ ndipo ndinachita zimenezi chifukwa cha inu, anthu ovutika a mʼgulu la nkhosali. Choncho ndinatenga ndodo ziwiri. Ina ndinaipatsa dzina lakuti Wosangalatsa ndipo inayo ndinaipatsa dzina lakuti Mgwirizano.+ Ndiyeno ndinayamba kuweta gulu la nkhosalo. 8 Ndinachotsa abusa atatu mʼmwezi umodzi chifukwa sindinathenso kuwalezera mtima ndipo iwonso ananyansidwa nane. 9 Ndipo ndinanena kuti: “Sindikuwetaninso. Amene akufa afe ndipo amene akuwonongeka, awonongeke. Otsalawo adyane.” 10 Choncho ndinatenga ndodo yanga yotchedwa Wosangalatsa+ ija nʼkuiduladula. Ndinachita izi kuti ndithetse pangano limene ndinachita ndi anthu a mtundu wanga. 11 Panganolo linaswedwa tsiku limenelo ndipo nkhosa zovutika zimene zinaona ndikuchita zimenezi, zinadziwa kuti zimene ndachitazo nʼzimene Yehova ananena.

12 Kenako ndinawauza kuti: “Ngati mukuona kuti nʼzoyenera, ndipatseni malipiro anga. Koma ngati mukuona kuti nʼzosayenera musandipatse.” Iwo anandilipira* ndalama 30 zasiliva.+

13 Kenako Yehova anandiuza kuti: “Kaziponye mosungiramo chuma. Zimenezi ndi ndalama zochepa zimene aona kuti angandilipire.”+ Choncho ndinatenga ndalama 30 zasilivazo nʼkukaziponya mosungiramo chuma panyumba ya Yehova.+

14 Kenako ndinathyola ndodo yanga yachiwiri ija yotchedwa Mgwirizano,+ pothetsa ubale wa Yuda ndi Isiraeli.+

15 Ndiyeno Yehova anandiuza kuti: “Tenga zida za mʼbusa wopanda pake.+ 16 Chifukwa ndilola kuti mʼdzikoli mukhale mʼbusa wina. Mʼbusa ameneyu sadzasamalira nkhosa zimene zikuwonongeka.+ Iye sadzafunafuna nkhosa yaingʼono, sadzachiritsa yovulala+ komanso sadzapatsa chakudya nkhosa zimene zikadali zamphamvu. Mʼmalomwake adzadya nyama ya nkhosa yonenepa+ ndipo adzakupula* ziboda za nkhosazo.+

17 Tsoka kwa mʼbusa wanga wopanda pake+ amene akusiya nkhosa.+

Lupanga lidzamutema padzanja ndi diso lake lakumanja.

Dzanja lake lidzalumala kwambiri,

Ndipo diso lake lamanja lidzachita khungu.”*

12 Uthenga wokhudza Isiraeli:

“Awa ndi mawu a Yehova okhudza Isiraeli.”

Yehova, amene anatambasula kumwamba,+

Amene anayala maziko a dziko lapansi,+

Komanso amene anapanga mzimu* umene uli mwa munthu, wanena kuti:

2 “Yerusalemu ndimusandutsa kapu imene imachititsa anthu a mitundu yonse yomuzungulira kuyenda dzandidzandi. Ndipo mdani adzazungulira Yuda komanso Yerusalemu.+ 3 Pa tsiku limenelo, Yerusalemu ndidzamusandutsa mwala wolemera* kwa anthu a mitundu yonse. Onse onyamula mwala umenewo, adzavulala koopsa.+ Anthu a mitundu yonse yapadziko lapansi adzasonkhana kuti amuukire.+ 4 Pa tsiku limenelo, ndidzachititsa kuti hatchi iliyonse ipanikizike ndipo wokwera pahatchiyo ndidzamuchititsa misala. Maso anga adzakhala panyumba ya Yuda, koma hatchi iliyonse ya anthu a mitundu ina ndidzaichititsa khungu,” watero Yehova. 5 “Mafumu a Yuda adzanena mumtima mwawo kuti, ‘Anthu a ku Yerusalemu akutipatsa mphamvu chifukwa Yehova wa magulu ankhondo akumwamba ndi Mulungu wawo.’+ 6 Pa tsiku limenelo, ndidzachititsa mafumu a Yuda kukhala ngati mbaula zamoto pakati pa mitengo komanso ngati miyuni yamoto pamilu ya tirigu.+ Iwo adzatentha anthu a mitundu yonse yowazungulira, kumanja ndi kumanzere.+ Ndipo anthu a ku Yerusalemu adzakhalanso pamalo awo mumzinda wa Yerusalemu.+

7 Yehova adzayamba nʼkupulumutsa matenti a Yuda. Adzachita zimenezi kuti kukongola* kwa nyumba ya Davide ndi kukongola* kwa anthu a ku Yerusalemu, kusakhale kwakukulu kwambiri kuposa kwa Yuda. 8 Pa tsiku limenelo, Yehova adzateteza anthu a ku Yerusalemu.+ Munthu amene wapunthwa* pa tsikulo, adzakhala wamphamvu ngati Davide. Nyumba ya Davide idzawatsogolera ngati Mulungu ndiponso ngati mngelo wa Yehova.+ 9 Ndipo pa tsikulo, ndidzatsimikiza kuwononga mitundu yonse ya anthu yobwera kudzaukira Yerusalemu.+

10 Anthu a mʼnyumba ya Davide ndiponso a ku Yerusalemu ndidzawapatsa mzimu wanga posonyeza kuti ndawakomera mtima ndipo udzawalimbikitsa kundipempha mochonderera. Iwo adzayangʼana kwa munthu amene anamubaya,+ ndipo adzamulirira ngati mmene angachitire polirira mwana yekhayo wamwamuna. Adzamulira kwambiri ngati akulira maliro a mwana wamwamuna woyamba kubadwa. 11 Pa tsiku limenelo, anthu adzalira kwambiri mu Yerusalemu ngati mmene analirira ku Hadadirimoni, mʼchigwa cha Megido.+ 12 Anthu amʼdziko lonselo adzalira mokuwa. Banja lililonse lizidzalira palokha. Banja la nyumba ya Davide lizidzalira palokha ndipo akazi a mʼbanjali azidzalira paokha. Banja la nyumba ya Natani+ lizidzalira palokha, ndipo akazi a mʼbanjali azidzalira paokha. 13 Banja la nyumba ya Levi+ lizidzalira palokha, ndipo akazi a mʼbanjali azidzalira paokha. Anthu a mʼbanja la Simeyi+ azidzalira paokha, ndipo akazi a mʼbanjali azidzalira paokha. 14 Mabanja onse otsala adzalira. Banja lililonse lizidzalira palokha, ndipo akazi a mʼmabanjawo azidzalira paokha.”

13 “Pa tsiku limenelo, a mʼnyumba ya Davide ndi anthu okhala mu Yerusalemu adzawakumbira chitsime kuti ayeretsedwe ku machimo awo.”+

2 Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti, “Pa tsiku limenelo, ndidzafufuta mayina a mafano mʼdziko lonseli+ ndipo sadzakumbukiridwanso. Ndidzachotsamo aneneri+ komanso mzimu wonyansa. 3 Munthu aliyense akadzayamba kulosera, bambo ake ndi mayi ake amene anamubereka adzamuuza kuti, ‘Iwe ufa ndithu, chifukwa walankhula zonama mʼdzina la Yehova.’ Ndiyeno bambo ndi mayi akewo adzamulasa chifukwa choti akulosera.+

4 Pa tsikulo, mneneri aliyense azidzachita manyazi ndi masomphenya ake pamene akulosera. Sadzavalanso chovala chapadera chaubweya+ kuti anamize anthu. 5 Ndipo azidzanena kuti, ‘Ine siine mneneri. Ndine mlimi, chifukwa munthu wina anandigula ndili wamngʼono.’ 6 Akadzafunsidwa kuti, ‘Kodi mabala amene ali pakati pa mapewa akowa* watani?’ Iye azidzayankha kuti, ‘Mabalawa anabwera chifukwa chomenyedwa kunyumba kwa anzanga.’”*

 7 “Iwe lupanga, nyamuka ubaye mʼbusa wanga.+

Ubaye munthu yemwe ndi mnzanga,” watero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.

“Ipha mʼbusa+ ndipo nkhosa zake zibalalike.+

Ine ndidzalanga nkhosa zonyozeka.”

 8 Yehova wanena kuti, “Mʼdziko lonseli,

Anthu awiri pa anthu atatu alionse adzaphedwa.

Ndipo wachitatuyo ndi amene adzatsale.”

 9 “Ine ndidzatenga anthu otsalawo nʼkuwaika pamoto.

Ndipo ndidzawayenga ngati mmene amayengera siliva

Komanso kuwayesa ngati mmene amayesera golide.+

Iwo adzaitana dzina langa,

Ndipo ine ndidzawayankha.

Ndidzanena kuti, ‘Awa ndi anthu anga,’+

Ndipo iwo adzanena kuti, ‘Yehova ndi Mulungu wathu.’”

14 “Tamverani! Tsiku la Yehova likubwera pamene adani anu adzakulandani zinthu zanu nʼkuzigawana ali mumzinda wanu womwewo. 2 Ndidzasonkhanitsa anthu a mitundu yonse kuti amenyane ndi Yerusalemu. Mzindawu udzalandidwa, katundu wamʼnyumba adzatengedwa ndipo akazi adzagwiriridwa. Hafu ya anthu amumzindawu idzatengedwa kupita kudziko lina, koma anthu otsalawo sadzachotsedwa mumzindawu.

3 Yehova adzapita kukamenyana ndi anthu a mitundu inawo+ ngati mmene amachitira pa tsiku la nkhondo.+ 4 Pa tsiku limenelo mapazi ake adzaponda paphiri la Maolivi+ lomwe lili moyangʼanizana ndi Yerusalemu mbali yakumʼmawa. Phirili lidzagawanika pakati kuyambira kumʼmawa mpaka kumadzulo* ndipo pakati pake padzakhala chigwa chachikulu kwambiri. Hafu ya phirilo idzasunthira kumpoto ndipo hafu inayo idzasunthira kumʼmwera. 5 Inu mudzathawira kuchigwa chimene chidzakhale pakati pa mapiri anga, chifukwa chigwacho chidzafika mpaka ku Azeli. Mudzathawa ngati mmene munathawira chivomerezi chimene chinachitika mʼmasiku a Uziya, mfumu ya Yuda.+ Ndipo Yehova Mulungu wanga adzabwera limodzi ndi oyera onse.+

6 Pa tsiku limenelo, sipadzakhala kuwala kwapadera.+ Zinthu zidzaundana chifukwa cha kuzizira. 7 Lidzakhala tsiku limodzi lotchedwa tsiku la Yehova.+ Sikudzakhala masana kapena usiku, chifukwa ngakhale usiku kudzakhala kukuwalabe. 8 Pa tsikulo madzi amoyo+ adzatuluka mu Yerusalemu.+ Hafu ya madziwo idzapita kunyanja yakumʼmawa*+ ndipo hafu inayo idzapita kunyanja ya kumadzulo.*+ Zimenezi zidzachitika mʼnyengo yotentha ndiponso mʼnyengo yozizira. 9 Yehova adzakhala Mfumu ya dziko lonse lapansi.+ Pa tsiku limenelo, Yehova adzakhala mmodzi+ ndipo dzina lake lidzakhala limodzi.+

10 Dziko lonse lidzakhala ngati chigwa cha Araba,+ kuyambira ku Geba+ kukafika ku Rimoni+ kumʼmwera kwa Yerusalemu. Mzindawu udzakwezedwa pamalo ake ndipo anthu adzakhalamo,+ kuyambira ku Geti la Benjamini+ mpaka ku Geti Loyamba nʼkukafika ku Geti la Pakona. Komanso adzakhala kuyambira ku Nsanja ya Hananeli+ mpaka kukafika kumalo a mfumu oponderamo mphesa. 11 Anthu adzakhala mumzindawo ndipo sudzatembereredwanso kuti uwonongedwe.+ Anthu azidzakhala mu Yerusalemu motetezeka.+

12 Mliri umene Yehova adzagwetsere anthu onse a mitundu ina amene amamenyana ndi Yerusalemu+ ndi uwu: Munthu aliyense mnofu wake udzawola ali chiimire, maso ake adzawola ali mʼmalo mwake ndiponso lilime lake lidzawola mʼkamwa mwake.

13 Pa tsiku limenelo Yehova adzawasokoneza kwambiri. Aliyense adzagwira dzanja la mnzake ndipo aliyense adzamenya mnzake.+ 14 Nayenso Yuda adzamenya nawo nkhondo ya ku Yerusalemu ndipo chuma cha anthu a mitundu yonse yowazungulira chidzasonkhanitsidwa. Adzasonkhanitsa golide, siliva ndi zovala zambirimbiri.+

15 Mliri wofanana ndi umenewu udzagweranso mahatchi, nyulu,* ngamila, abulu komanso ziweto zonse zimene zidzapezeke mʼmisasa ya adaniwo.

16 Aliyense wotsala mwa anthu a mitundu yonse obwera kudzamenyana ndi Yerusalemu, chaka chilichonse+ azidzapita kukagwadira* Mfumu, Yehova wa magulu ankhondo akumwamba,+ ndiponso kukachita nawo Zikondwerero za Misasa.+ 17 Koma mvula sidzagwa mʼdziko la munthu aliyense wochokera mʼmabanja apadziko lapansi, amene sadzapita ku Yerusalemu kukagwadira Mfumu, Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.+ 18 Ngati anthu a ku Iguputo sadzabwera mumzindawu, mʼdziko lawonso simudzagwa mvula. Mʼmalomwake, Yehova adzawagwetsera mliri umene amagwetsera anthu a mitundu ina amene sabwera kudzachita Zikondwerero za Misasa. 19 Chimenechi chidzakhala chilango cha tchimo la Iguputo komanso mitundu yonse imene sibwera kudzachita nawo Zikondwerero za Misasa.

20 Pa tsiku limenelo, pamabelu a mahatchi padzalembedwa mawu akuti ‘Chiyero nʼcha Yehova!’+ Ndipo miphika yakukamwa kwakukulu+ yamʼnyumba ya Yehova idzakhala ngati mbale zolowa+ zapaguwa lansembe. 21 Mphika uliwonse wakukamwa kwakukulu mu Yerusalemu ndi mu Yuda udzakhala woyera ndipo udzakhala wa Yehova wa magulu ankhondo akumwamba. Anthu onse amene azidzapereka nsembe azidzatenga ina mwa miphikayo nʼkuphikiramo. Pa tsiku limenelo, mʼnyumba ya Yehova wa magulu ankhondo akumwamba simudzapezeka munthu wa ku Kanani.”*+

Kutanthauza “Yehova Wakumbukira.”

Onani Zakumapeto B15.

Ena amati “hosi.”

Nʼkuthekanso kuti panali hatchi yofiira kwambiri, yofiirira ndi yoyera.

Kapena kuti, “mphamvu.”

Mawu akuti “mwana wamkazi wa Babulo” ndi mawu andakatulo ndipo nthawi zambiri amanena za mzinda wa Babulo kapena anthu amene ankakhala mumzindawo.

Mawu akuti “mwana wamkazi wa Ziyoni” ndi mawu andakatulo ndipo nthawi zambiri amanena za mzinda wa Yerusalemu kapena anthu amene ankakhala mumzindawo.

Kapena kuti, “mikanjo yapadera.”

Kapena kuti, “uzidzayangʼanira; uzidzalondera.”

Mabaibulo ena amati, “Maso 7 amenewa.”

Kapena kuti, “nthambi zolemedwa ndi zipatso.”

Mkono umodzi ndi wofanana ndi masentimita 44 ndi hafu. Onani Zakumapeto B14.

Chiwiya chimenechi chinali basiketi yomwe ankagwiritsa ntchito poyeza muyezo wa efa. Muyezo wa efa ndi ofanana ndi malita 22. Onani Zakumapeto B14.

Mʼchilankhulo choyambirira, “pakati pa dziko lapansi ndi kumwamba.”

Kumeneku ndi ku Babeloniya.

Kapena kuti, “amkuwa.”

Kapena kuti, “chisoti chachifumu cholemekezeka.”

Kapena kuti, “chisoti chachifumu cholemekezekacho.”

Onani Zakumapeto B15.

Kapena kuti, “akakhazike pansi mtima wa Yehova.”

Kapena kuti, “apakachisi.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “ndilire.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mwana wamwamuna wopanda bambo.”

Mabaibulo ena amati, “mwala wolimba kwambiri.”

Kapena kuti, “malangizo.”

Kapena kuti, “wokhulupirika.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “chifukwa cha kuchuluka kwa masiku.”

Kapena kuti, “wokhulupirika.”

Kapena kuti, “timukhazike mtima pansi.”

Kapena kuti, “timukhazike mtima pansi.”

Kapena kuti, “mʼmunsi mwa chovala.”

Kapena kuti, “amene ankawapondereza.”

Mwina kutanthauza kuvutika kwa anthu ake.

Mawu akuti “mwana wamkazi wa Ziyoni” ndi mawu andakatulo ndipo nthawi zambiri amanena za mzinda wa Yerusalemu kapena anthu amene ankakhala mumzindawo.

Mawu akuti “mwana wamkazi wa Yerusalemu” ndi mawu andakatulo ndipo nthawi zambiri amanena za mzinda wa Yerusalemu kapena anthu amene ankakhala mumzindawo.

Kapena kuti, “yapambana; yapulumutsidwa.”

Umenewu ndi mtsinje wa Firate.

Gulaye ndi chipangizo choponyera miyala chimene amachita kupukusa ndi dzanja.

Kapena kuti, “Milungu ya banja; Mafano.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “okhala ngati atonde a mbuzi.”

Kapena kuti, “Kapitawo.”

Mtengo wa junipa ndi wofanana ndi mtengo wa mkungudza.

Ena amati, “nthundu.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “anandiyezera.”

Ena amati, “kusupula.”

Kapena kuti, “lidzachita mdima.”

Kapena kuti, “mpweya.”

Kapena kuti, “wotopetsa.”

Kapena kuti, “ulemerero.”

Kapena kuti, “ulemerero.”

Kapena kuti, “wafooka kwambiri.”

Nʼkutheka kuti mabalawo ali pamtima kapena kumsana.

Kapena kuti, “anthu ondikonda.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “kunyanja.”

Imeneyi ndi Nyanja Yakufa.

Imeneyi ndi nyanja ya Mediterranean.

“Nyulu” ndi nyama yooneka ngati hatchi.

Kapena kuti, “kukalambira.”

Mabaibulo ena amati, “simudzapezeka wamalonda.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena