1 Samueli
25 Patapita nthawi, Samueli+ anamwalira ndipo Aisiraeli onse anasonkhana pamodzi ndi kulira+ maliro ake. Iwo anamuika m’manda panyumba yake ku Rama.+ Kenako Davide ananyamuka ndi kupita kuchipululu cha Parana.+
2 Tsopano mwamuna wina anali kukhala ku Maoni,+ koma ntchito yake anali kugwirira ku Karimeli.*+ Mwamuna ameneyu anali wotchuka kwambiri, ndipo anali ndi nkhosa 3,000 ndi mbuzi 1,000. Tsiku lina, iye anali kugwira ntchito yometa ubweya+ wa nkhosa zake ku Karimeli. 3 Mwamuna ameneyu dzina lake anali Nabala,+ ndipo mkazi wake anali Abigayeli.+ Mkazi wakeyu anali wanzeru kwambiri+ ndi wokongola, koma mwamunayu anali wouma mtima ndi wokonda kuchita zinthu zoipa.+ Mwamuna ameneyu anali wa m’banja la Kalebe.+ 4 Davide ali kuchipululu, anamva kuti Nabala akumeta ubweya+ wa nkhosa zake. 5 Choncho Davide anatumiza anyamata ake 10 ndi kuwauza kuti: “Pitani ku Karimeli kwa Nabala mukam’funse za moyo wake m’dzina langa.+ 6 M’bale wangayo mukamuuze kuti, ‘Mtendere ukhale nawe+ pamodzi ndi onse a m’nyumba yako ndi zonse zimene uli nazo. 7 Ine ndamva kuti ukumeta ubweya wa nkhosa zako. Abusa ako anali ndi ife.+ Sitinawavutitse,+ ndipo masiku onse amene tinali nawo ku Karimeli, palibe kanthu kawo kamene kanasowa. 8 Funsa anyamata ako zimenezi ndipo akuuza. Motero uwakomere mtima anyamata anga chifukwa tabwera tsiku labwino. Chonde, ugawire atumiki ako ndi mwana wako Davide chilichonse chimene dzanja lako lingapeze.’”+
9 Chotero anyamata a Davide anapita kukauza Nabala mawu onsewa m’dzina la Davide ndi kuyembekezera. 10 Pamenepo Nabala anayankha atumiki a Davide kuti: “Kodi Davide ndani,+ ndipo mwana wa Jese ndani? Masiku ano atumiki amene akuthawa ambuye awo achuluka kwabasi.+ 11 Ndiye ine nditenge mkate wanga,+ madzi ndi nyama imene ndaphera anyamata anga ometa ubweya wa nkhosa n’kupereka kwa amuna amene sindikudziwa m’pang’ono pomwe kumene achokera?”+
12 Atamva zimenezi, anyamata a Davide anatembenuka ndi kubwerera, ndipo atafika anamuuza mawu onsewa. 13 Nthawi yomweyo, Davide anauza amuna amene anali kuyenda naye kuti: “Aliyense amange lupanga lake m’chiuno!”+ Pamenepo aliyense anamangadi lupanga lake m’chiuno, ndipo Davide nayenso anamanga lupanga lake m’chiuno. Zitatero, amuna pafupifupi 400 anapitira limodzi ndi Davide, koma amuna 200 anatsala kuti ayang’anire katundu.+
14 Izi zili choncho, mmodzi mwa anyamata a Nabala anauza Abigayeli, mkazi wa Nabala kuti: “Davide anatumiza nthumwi zake kuchokera m’chipululu kudzafunira zabwino mbuyanga, koma mbuyanga walalatira+ nthumwizo. 15 Amuna amenewa anatichitira zabwino kwambiri, sanativutitse, moti masiku onse amene tinali kuyenda nawo kutchire sitinataye kanthu ngakhale kamodzi.+ 16 Iwo anali ngati khoma+ lotizungulira usana ndi usiku, masiku onse amene tinakhala nawo pamene tinali kuweta nkhosa. 17 Choncho mudziwe zimenezi ndi kuona zimene mungachite, chifukwa atsimikiza kudzetsa tsoka+ pa mbuyanga ndi onse a m’nyumba yake, pakuti mbuye wathu ndi munthu wopanda pake,+ sitingathe kulankhula naye.”
18 Nthawi yomweyo, Abigayeli+ anafulumira kutenga mitanda 200 ya mkate, mitsuko iwiri ikuluikulu ya vinyo,+ anapha nkhosa zisanu,+ anatenganso miyezo ya seya* isanu ya tirigu wokazinga,+ mphesa zouma zoumba pamodzi 100+ ndi nkhuyu zouma zoumba pamodzi 200+ ndi kuzikweza pa abulu. 19 Kenako anauza anyamata ake kuti: “Tsogolani,+ ine ndikubwera m’mbuyo mwanu.” Koma mwamuna wake Nabala sanamuuze kalikonse.
20 Ndiyeno pamene Abigayeli anali kutsika phiri atakwera bulu,+ mwadzidzidzi, anaona Davide ndi amuna amene anali kuyenda naye akubwera, ndipo iye anakumana nawo. 21 Davide anali atanena kuti: “Ine ndinalondera zinthu zake m’chipululu ndipo palibe chinthu chake ngakhale chimodzi chimene chinasowa.+ N’zokhumudwitsa kuti munthu ameneyu akundibwezera zoipa pa zabwino zimene ndinam’chitira.+ 22 Choncho Mulungu alange mowirikiza+ adani a Davide, ngati ine ndidzasiya munthu aliyense wa m’nyumba ya Nabala wokodzera khoma*+ ali wamoyo kufikira m’mawa.”+
23 Abigayeli ataona Davide, nthawi yomweyo anatsika mofulumira pabulu wake. Iye anagwada pamaso pa Davide ndi kuwerama mpaka nkhope yake pansi.+ 24 Kenako anagwada pamapazi+ a Davide ndi kunena kuti: “Zolakwa zonse zikhale pa ine+ mbuyanga. Chonde, lolani kapolo wanu wamkazi alankhule nanu+ ndipo mvetserani mawu a kapolo wanu. 25 Chonde mbuyanga, musaganizire za Nabala, munthu wopanda pakeyu,+ chifukwa zochita zake ndi zogwirizana ndi dzina lake. Dzina lake ndi Nabala* ndipo ndi wopandadi nzeru.+ Koma ine kapolo wanu wamkazi sindinawaone anyamata amene inu mbuyanga munawatuma. 26 Tsopano mbuyanga, ndikulumbira pali Yehova, Mulungu wamoyo,+ komanso pali moyo wanu:+ Yehova wakubwezani+ kuti musapalamule mlandu wamagazi+ komanso kuti musadzipulumutse nokha ndi dzanja lanu.+ Choncho lolani kuti adani anu ndi onse ofuna kukuvulazani mbuyanga, akhale ngati Nabala.+ 27 Ndiyeno mphatso*+ imene kapolo wanu wamkazi wabweretsa kwa inu mbuyanga, muipereke kwa anyamata amene akutsatira mapazi anu.+ 28 Chonde, khululukani kulakwa kwa kapolo wanu wamkazi,+ pakuti mosalephera Yehova adzakukhazikitsirani nyumba yachifumu, inu mbuyanga, ndipo idzakhalapo kwa nthawi yaitali,+ chifukwa inu mbuyanga mukumenya nkhondo za Yehova.+ Ndipo mwa inu simudzapezeka choipa chilichonse masiku onse a moyo wanu.+ 29 Munthu akakuukirani ndi kufunafuna moyo wanu, Yehova Mulungu+ adzakulunga ndi kuteteza moyo wanu m’phukusi la moyo+ monga mmene munthu amatetezera chuma chake. Koma moyo wa adani anu adzauponya ndi kuutaya kutali ngati mmene munthu amaponyera mwala ndi gulaye.*+ 30 Ndiye zimene zidzachitika n’zakuti, chifukwa chakuti Yehova adzachitira inu mbuyanga zabwino zimene wanena kwa inu, iye adzakuikani kukhala mtsogoleri wa Isiraeli.+ 31 Choncho musalole kuti zimenezi zikhale zokuvutitsani chikumbumtima ndi zokhumudwitsa mumtima mwanu mbuyanga, mwa kukhetsa magazi popanda chifukwa+ ndi kudzipulumutsa nokha ndi dzanja lanu.+ Mukatero, Yehova adzakuchitirani zabwino mbuyanga, ndipo mudzandikumbukire+ ine kapolo wanu wamkazi.”
32 Pamenepo Davide anauza Abigayeli kuti: “Adalitsike Yehova Mulungu wa Isiraeli,+ amene wakutumiza kudzakumana nane lero! 33 Iwenso udalitsike chifukwa cha kulingalira bwino kwako.+ Udalitsike chifukwa cha kundigwira lero kuti ndisapalamule mlandu wamagazi+ ndi kudzipulumutsa ndekha ndi dzanja langa.+ 34 Komabe, pali Yehova Mulungu wamoyo wa Isiraeli, amene wandigwira kuti ndisakuchitire choipa,+ ukanapanda kufulumira kudzakumana nane,+ ndithu sipakanatsala munthu wokodzera khoma+ m’banja la Nabala pofika mawa m’mawa.” 35 Atatero, Davide analandira zimene Abigayeli anamubweretsera ndiyeno anamuuza kuti: “Pita kunyumba kwako mwamtendere.+ Taona, ndamvera mawu ako kuti ndichite zinthu mokuganizira.”+
36 Kenako Abigayeli anapita kwa Nabala ndipo anapeza kuti akuchita phwando m’nyumba mwake ngati phwando la mfumu.+ Nabala anali kusangalala kwambiri mumtima mwake ndipo anali ataledzereratu.+ Abigayeli sanamuuze chilichonse, chaching’ono kapena chachikulu, kufikira m’mawa mwake. 37 Tsopano m’mawa mwake, vinyo atamuthera m’mutu, mkazi wake anayamba kumuuza zinthu zonsezi. Nabala atamva zimenezi, mtima wake+ unaferatu mkati mwake ndipo iye anakhala ngati mwala. 38 Patapita masiku 10, Yehova anakantha+ Nabala ndipo anafa.
39 Ndiyeno Davide anamva kuti Nabala wamwalira. Atatero, iye anati: “Adalitsike Yehova amene wandiweruzira mlandu+ ndi kundimasula ku chitonzo+ cha Nabala, komanso wagwira ine mtumiki wake kuti ndisachite choipa.+ Yehova wabwezera zoipa za Nabala pamutu pake!”+ Pamenepo Davide anatumiza anthu kuti akamufunsirire Abigayeli, kuti akhale mkazi wake.+ 40 Choncho atumiki a Davide anapita ku Karimeli ndi kulankhula naye kuti: “Davide watituma kwa iwe kuti tikutenge ukakhale mkazi wake.” 41 Nthawi yomweyo, ananyamuka ndi kugwada mpaka nkhope yake pansi,+ n’kunena kuti: “Ine kapolo wanu ndine wokonzeka kukhala mtumiki wosambitsa mapazi+ a atumiki a mbuyanga.”+ 42 Kenako Abigayeli+ ananyamuka mofulumira ndi kukwera pabulu,+ atsikana ake asanu antchito akumutsatira pambuyo. Iye anatsatira nthumwi za Davide ndipo anakakhala mkazi wake.
43 Davide anali atatenganso Ahinowamu+ wa ku Yezereeli,+ ndipo onse awiriwa anakhala akazi ake.+
44 Koma Sauli anali atapereka Mikala+ mwana wake wamkazi, mkazi wake wa Davide, kwa Paliti,+ mwana wamwamuna wa Laisi wa ku Galimu.+