Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • nwt Romans 1:1-16:27
  • Aroma

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Aroma
  • Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Aroma

KALATA YOPITA KWA AROMA

1 Ine Paulo kapolo wa Khristu Yesu, ndinaitanidwa kuti ndikhale mtumwi ndiponso ndinasankhidwa kuti ndilalikire uthenga wabwino wa Mulungu.+ 2 Iye analonjeza uthenga umenewu kalekale kudzera mwa aneneri ake mʼMalemba oyera. 3 Uthengawo umanena za Mwana wake, amene ndi mbadwa* ya Davide,+ 4 ndipo Mulungu anaukitsa Mwana+ wakeyu pogwiritsa ntchito mphamvu ya mzimu wake woyera. Ameneyu ndi Yesu Khristu Ambuye wathu. 5 Kudzera mwa iyeyu, Mulungu anatisonyeza kukoma mtima kwakukulu ndipo ndinasankhidwa kukhala mtumwi+ kuti ndikathandize anthu a mitundu yonse kuti asonyeze chikhulupiriro, akhale omvera+ ndiponso kuti alemekeze dzina lake. 6 Pakati pa anthu a mitundu imeneyo palinso inuyo amene munaitanidwa kuti mukhale otsatira a Yesu Khristu. 7 Kalatayi ndalembera inu nonse okhala ku Roma amene mumakondedwa ndi Mulungu komanso munaitanidwa kuti mukhale oyera:

Mukhale ndi kukoma mtima kwakukulu ndiponso mtendere wochokera kwa Mulungu Atate wathu ndi Ambuye wathu Yesu Khristu.

8 Choyamba, ndikuthokoza Mulungu wanga kudzera mwa Yesu Khristu chifukwa cha nonsenu, chifukwa anthu padziko lonse akunena za chikhulupiriro chanu. 9 Nthawi zonse ndikamapemphera ndimakutchulani mʼmapemphero anga ndipo Mulungu, amene ndikumuchitira utumiki wopatulika ndi mtima wanga wonse polalikira uthenga wabwino wonena za Mwana wake, akundichitira umboni.+ 10 Ndimamupempha kuti ngati nʼkotheka komanso ngati nʼzimene akufuna, ulendo uno wokha ndibwere kwanuko. 11 Chifukwa ndikulakalaka nditakuonani kuti ndikupatseni mphatso inayake yauzimu kuti mukhale olimba, 12 kapena kuti ndidzalimbikitsidwe ndi chikhulupiriro chanu, nanunso mudzalimbikitsidwe+ ndi chikhulupiriro changa.

13 Koma abale ndikufuna mudziwe kuti kwa nthawi yaitali ndakhala ndikufuna kubwera kwanuko, koma zakhala zikulephereka. Ndikufuna ndidzaone zotsatira zabwino za ntchito yathu yolalikira ngati mmene zilili pakati pa anthu a mitundu ina yonse. 14 Ineyo ndili ndi ngongole kwa Agiriki ndi kwa anthu amene si Agiriki komanso kwa anthu anzeru ndi kwa anthu opusa. 15 Choncho ndikufunitsitsa kudzalalikira uthenga wabwino kwa inunso kumeneko ku Roma.+ 16 Ine sindichita manyazi ndi uthenga wabwino.+ Kunena zoona, uthengawo ndi njira yamphamvu imene Mulungu akuigwiritsa ntchito pofuna kupulumutsa aliyense amene ali ndi chikhulupiriro,+ choyamba Ayuda+ kenako Agiriki.+ 17 Mu uthenga wabwinowu, Mulungu amaulula chilungamo chake kwa anthu amene ali ndi chikhulupiriro.+ Zikatero, chikhulupiriro cha anthuwo chimalimba mogwirizana ndi zimene Malemba amanena kuti: “Koma wolungama adzakhala ndi moyo chifukwa cha chikhulupiriro chake.”+

18 Kuchokera kumwamba, Mulungu akusonyeza mkwiyo wake+ kwa anthu onse osaopa Mulungu ndi ochita zoipa amene akuchititsa kuti choonadi chisadziwike.+ 19 Zili choncho chifukwa Mulungu wawapatsa umboni wokwanira wowathandiza kuti amudziwe.+ 20 Kuchokera pamene dziko linalengedwa, makhalidwe a Mulungu osaoneka ndi maso akuonekera bwino. Makhalidwe a Mulungu amenewa,+ ngakhalenso mphamvu zake zosatha+ ndiponso Umulungu wake,+ zikuonekera mʼzinthu zimene anapanga moti anthuwo alibenso chifukwa chomveka chosakhulupirira kuti kuli Mulungu. 21 Ngakhale kuti ankadziwa Mulungu, iwo sanamulemekeze monga Mulungu komanso sanamuthokoze. Mʼmalomwake anayamba kuganiza zinthu zopanda nzeru ndipo mitima yawo yopusayo inachita mdima.+ 22 Ngakhale amanena kuti ndi anzeru, iwo ndi opusa. 23 Mʼmalo molemekeza Mulungu yemwe sangafe, iwo amalemekeza zifaniziro za anthu omwe amafa komanso zifaniziro za mbalame, nyama za miyendo 4 ndiponso nyama zokwawa.+

24 Choncho mogwirizana ndi zilakolako zamʼmitima mwawo, Mulungu anawasiya kuti achite zonyansa, kuti achite zochititsa manyazi ndi matupi awo. 25 Choonadi chonena za Mulungu anachisinthanitsa ndi bodza ndipo amalambira ndiponso kutumikira chilengedwe mʼmalo mwa Mlengi amene ayenera kutamandidwa mpaka kalekale. Ame. 26 Ndiye chifukwa chake Mulungu anawasiya kuti atsatire zilakolako zosalamulirika za kugonana,+ popeza akazi pakati pawo anasiya njira yachibadwa ya matupi awo nʼkumachita zosemphana ndi chibadwa.+ 27 Amunanso chimodzimodzi. Iwo anasiya njira yachibadwa yofuna akazi nʼkumatenthetsana okhaokha mwachiwawa ndi chilakolako choipa, amuna okhaokha+ kuchitirana zonyansa nʼkulandiriratu mphoto yoyenerera kulakwa kwawo.+

28 Popeza sankaona kuti nʼzofunika kudziwa Mulungu molondola, iye anawasiya kuti apitirize kuganiza zoipa nʼkumachita zinthu zosayenera.+ 29 Ndipo ankachita zosalungama za mtundu ulionse,+ kuipa konse, dyera*+ ndiponso zinthu zonse zoipa. Mtima wawo unadzaza ndi kaduka,+ kupha anthu,+ ndewu, chinyengo+ ndi njiru.+ Ankakondanso miseche 30 ndiponso kujeda anzawo.+ Ankadana ndi Mulungu, anali achipongwe, odzikuza, odzitama, achiwembu, osamvera makolo,+ 31 osazindikira,+ osasunga mapangano, opanda chikondi chachibadwa ndiponso opanda chifundo. 32 Ngakhale kuti anthuwa amalidziwa bwino lamulo lolungama la Mulungu, lakuti amene amachita zinthu zimenezi ndi oyenera imfa,+ amapitiriza kuzichita. Kuwonjezera pamenepo, amagwirizananso ndi anthu amene amachita zimenezi.

2 Choncho kaya ndiwe ndani,+ ngati umaweruza ena, ulibe chifukwa chomveka chodzilungamitsira. Popeza ukamaweruza ena, umakhala ukudzitsutsa wekha, chifukwa iwenso umachita zomwezo.+ 2 Tikudziwa kuti Mulungu akamaweruza anthu amene amachita zimenezi kuti ndi oyenera kulandira chilango, amawaweruza mogwirizana ndi choonadi.

3 Koma iweyo ukamaweruza anthu amene amachita zinthu zimene iwenso umachita, kodi ukuganiza kuti udzazemba chiweruzo cha Mulungu? 4 Kodi sukudziwa kuti Mulungu akukusonyeza kukoma mtima kwake kwakukulu,+ kusakwiya msanga+ komanso kuleza mtima+ nʼcholinga choti ulape?+ 5 Koma chifukwa chakuti sukufuna kusintha, ndipo ukusonyeza mtima wosalapa, Mulungu adzakulanga ndithu pa tsiku la mkwiyo wake akamadzaulula chiweruzo chake cholungama.+ 6 Iye adzaweruza aliyense mogwirizana ndi zochita zake.+ 7 Adzapereka moyo wosatha kwa anthu amene akupitirizabe kuchita zabwino.+ Anthu amenewa akuyesetsa kupeza ulemerero, ulemu ndi moyo wosawonongeka. 8 Koma anthu amene amakonda mikangano, satsatira choonadi komanso amachita zosalungama, Mulungu adzawasonyeza mkwiyo wake.+ 9 Munthu aliyense wochita zoipa, kaya akhale Myuda kapena Mgiriki, adzakumana ndi mavuto komanso zowawa. 10 Koma aliyense wochita zabwino adzalandira ulemerero, ulemu ndi mtendere, choyamba Myuda+ kenako Mgiriki.+ 11 Chifukwa Mulungu alibe tsankho.+

12 Anthu onse amene anachimwa asakudziwa Chilamulo, adzafa asakudziwa Chilamulo.+ Koma onse amene anachimwa akudziwa Chilamulo, adzaweruzidwa mogwirizana ndi Chilamulocho.+ 13 Paja anthu ongomva Chilamulo, Mulungu samawaona kuti ndi olungama koma amene amatsatira Chilamulo ndi amene adzaonedwe kuti ndi olungama.+ 14 Anthu a mitundu ina alibe Chilamulo.+ Koma akamachita mwachibadwa zinthu zomwe zili mʼChilamulo, ngakhale kuti alibe Chilamulo, amasonyeza kuti ali ndi Chilamulo mumtima mwawo. 15 Amenewa amasonyeza kuti mfundo za mʼChilamulo zinalembedwa mʼmitima mwawo ndipo chikumbumtima chawo chimawachitira umboni. Anthu amenewa maganizo awo amawatsutsa kapenanso kuwavomereza. 16 Zimenezi zidzaonekera pa tsiku limene Mulungu, kudzera mwa Khristu Yesu, adzaweruze zinthu zachinsinsi zimene anthu amachita komanso kuganiza.+ Ndipo adzaweruza mogwirizana ndi uthenga wabwino umene ndikulalikira.

17 Enanu mumadzitchula kuti ndinu Ayuda,+ mumadalira Chilamulo ndiponso mumadzitama kuti muli pa ubwenzi ndi Mulungu. 18 Mumadziwa zimene Mulungu amafuna komanso mumasangalala ndi zinthu zabwino kwambiri chifukwa chakuti munaphunzitsidwa Chilamulo.+ 19 Mumakhulupirira kuti mungathe kutsogolera akhungu komanso kuunikira anthu amene ali mumdima. 20 Mumaganiza kuti mungathe kuwongolera anthu opanda nzeru. Mumaganizanso kuti mungathe kuphunzitsa ana chifukwa mumamvetsa komanso kudziwa choonadi chopezeka mʼChilamulo. 21 Kodi iwe amene umaphunzitsa ena, bwanji sudziphunzitsa wekha?+ Umalalikira kuti, “Usabe,”+ ndiye iwe umabanso? 22 Iwe amene umanena kuti, “Usachite chigololo,”+ kodi umachitanso chigololo? Iweyo amene umalankhula zosonyeza kuti umanyansidwa ndi mafano, ndiye umabanso zamʼkachisi? 23 Iwe wonyadira Chilamulo, kodi umachitiranso Mulungu chipongwe pophwanya Chilamulo? 24 “Dzina la Mulungu likunyozedwa pakati pa anthu amitundu ina chifukwa cha inu,” ngati mmene Malemba amanenera.+

25 Mdulidwe+ ndi waphindu pokhapokha ngati iweyo umatsatiradi Chilamulo.+ Koma ngati umaphwanya Chilamulo, mdulidwe wako ndi wopanda ntchito. 26 Choncho ngati munthu wosadulidwa+ akutsatira mfundo zolungama za mʼChilamulo, kusadulidwa kwake kudzaonedwa ngati kudulidwa, si choncho?+ 27 Munthu amene ndi wosadulidwa akamatsatira Chilamulo, adzakuweruza. Adzakuweruza iweyo amene umaphwanya Chilamulo ngakhale kuti uli ndi malamulo olembedwa ndiponso ndiwe wodulidwa. 28 Amene ali Myuda kunja kokha si Myuda,+ ndiponso mdulidwe wakunja kokha wochitidwa pathupi, si mdulidwe.+ 29 Kukhala Myuda weniweni kuli mumtima+ ndipo mdulidwe wake umakhalanso wamumtima+ wochitidwa ndi mzimu, osati ndi malamulo olembedwa.+ Munthu woteroyo amatamandidwa ndi Mulungu, osati anthu.+

3 Kodi kukhala Myuda kuli ndi ubwino wotani, kapena phindu la mdulidwe nʼchiyani? 2 Ubwino wake ndi wambiri. Choyamba, mawu opatulika a Mulungu anaikidwa mʼmanja mwa Ayuda.+ 3 Nanga bwanji ngati ena anali osakhulupirika? Kodi kupanda chikhulupiriro kwawoko kukutanthauza kuti Mulungunso ndi wosakhulupirika? 4 Ayi. Ngakhale munthu aliyense atakhala wabodza,+ Mulungu angapezekebe kuti ndi wonena zoona+ mogwirizana ndi zimene Malemba amanena kuti: “Mukamalankhula, mumalankhula zachilungamo kuti muwine pamene mukuweruzidwa.”+ 5 Komabe ngati kusalungama kwathu kukusonyeza bwino kuti Mulungu ndi wolungama, ndiye tinene kuti chiyani? Kodi tingati Mulungu ndi wosalungama akamaonetsa mkwiyo wake? (Ndikulankhula ngati mmene anthu ena amalankhulira.) 6 Ayi! Nanga Mulungu akapanda kutero, dziko adzaliweruza bwanji?+

7 Koma ngati chifukwa cha bodza langa choonadi cha Mulungu chaonekera kwambiri ndipo zimenezo zamubweretsera ulemerero, nʼchifukwa chiyani ndikuweruzidwa ngati wochimwa? 8 Ndilekerenji kunena zimene ena amatinamizira kuti timanena zija, zakuti: “Tiyeni tichite zoipa kuti pakhale zinthu zabwino”? Anthu amene amanena zimenezi adzaweruzidwa mogwirizana ndi chilungamo.+

9 Ndiye kodi zikatero Ayudafe tili pabwino kuposa ena? Ayi ndithu. Chifukwa monga tanena kale, Ayuda ndiponso Agiriki, onse amalamuliridwa ndi uchimo+ 10 mogwirizana ndi zimene Malemba amanena kuti: “Palibe munthu wolungama ndi mmodzi yemwe.+ 11 Palibe amene ali wozindikira ngakhale pangʼono komanso palibe amene akuyesetsa kufunafuna Mulungu. 12 Anthu onse apatuka, ndipo onse akhala opanda pake. Palibiretu ndi mmodzi yemwe amene akusonyeza kukoma mtima.”+ 13 “Mmero wawo* ndi manda otseguka. Iwo amalankhula zachinyengo ndi lilime lawo.”+ “Mʼmilomo yawo muli poizoni wa njoka.”+ 14 “Ndipo mʼkamwa mwawo mwadzaza matemberero ndi mawu opweteka.”+ 15 “Mapazi awo amathamangira kukakhetsa magazi.”+ 16 “Zonse zimene amachita zimakhala zowononga ndiponso zobweretsa mavuto, 17 ndipo njira ya mtendere sakuidziwa.”+ 18 “Maso awo saona chifukwa choopera Mulungu.”+

19 Tikudziwa kuti zinthu zonse zimene Chilamulo chimanena zimagwira ntchito kwa amene amatsatira Chilamulo. Cholinga chake nʼkuchititsa anthu kuti asowe chonamizira komanso kusonyeza kuti dziko lonse lili ndi mlandu pamaso pa Mulungu ndipo ndi loyenera kulandira chilango.+ 20 Choncho palibe munthu amene amaonedwa wolungama ndi Mulungu chifukwa chotsatira Chilamulo,+ popeza Chilamulo chimatithandiza kudziwa bwino uchimo.+

21 Koma tsopano, zadziwika kuti munthu akhoza kukhala wolungama kwa Mulungu popanda kutsatira Chilamulo.+ Zimenezi zinatchulidwanso mʼChilamulo komanso zimene aneneri analemba.+ 22 Kuonedwa wolungama ndi Mulungu kumeneku kungatheke kwa onse amene amasonyeza kuti amakhulupirira Yesu Khristu, chifukwa palibe kusiyana.+ 23 Popeza anthu onse ndi ochimwa ndipo amalephera kusonyeza bwinobwino ulemerero wa Mulungu.+ 24 Ndipo kuonedwa olungama chifukwa cha kukoma mtima kwake kwakukulu+ kumene wakusonyeza powamasula ndi dipo lolipiridwa ndi Khristu Yesu,+ kuli ngati mphatso yaulere.+ 25 Mulungu anamupereka ngati nsembe yoti anthu agwirizanenso ndi Mulunguyo+ pokhulupirira magazi ake.+ Anachita zimenezi pofuna kuonetsa chilungamo chake chifukwa anasonyeza kuti ndi wosakwiya msanga pokhululuka machimo amene anachitika kale. 26 Anachita zimenezi kuti asonyeze chilungamo chake+ pa nthawi inoyo poona kuti munthu amene amakhulupirira Yesu ndi wolungama.+

27 Choncho, kodi pamenepa palinso chifukwa chodzitamira? Palibetu. Kodi tizidzitama chifukwa chotsatira Chilamulo?+ Ndithudi ayi, koma chifukwa chotsatira lamulo la chikhulupiriro. 28 Taona kuti munthu amakhala wolungama mwa chikhulupiriro, osati potsatira Chilamulo.+ 29 Kapena kodi iye ndi Mulungu wa Ayuda okha?+ Kodi si Mulungu wa anthu a mitundu inanso?+ Inde, iye ndi Mulungunso wa anthu a mitundu ina.+ 30 Popeza Mulungu ndi mmodzi,+ iye adzaona kuti anthu odulidwa ndi olungama+ chifukwa cha chikhulupiriro chawo. Adzaonanso kuti anthu osadulidwa ndi olungama+ chifukwa cha chikhulupiriro chawo. 31 Kodi pamenepa tikuthetsa Chilamulo mwa chikhulupiriro chathu? Ayi! Mʼmalomwake, tikulimbikitsa Chilamulo.+

4 Popeza zili choncho, kodi tinene chiyani za kholo lathu Abulahamu? 2 Mwachitsanzo, zikanakhala kuti Abulahamu ankaonedwa kuti ndi wolungama chifukwa cha zimene anachita, akanakhala ndi chifukwa chodzitamira, koma osati pamaso pa Mulungu. 3 Kodi paja Malemba amati chiyani? Amati: “Abulahamu anakhulupirira zimene Yehova* anamuuza, ndipo anaonedwa kuti ndi wolungama.”+ 4 Munthu amene wagwira ntchito saona malipiro ake ngati kukoma mtima kwakukulu, koma ngati zimene amayenera kulandira.* 5 Koma Mulungu amene amaona anthu ochimwa kukhala olungama amaona kuti munthu yemwe sanagwire ntchito, koma amamukhulupirira, ndi wolungama.+ 6 Davide ananena za munthu wosangalala amene Mulungu amamuona kuti ndi wolungama ngakhale kuti zimene wachita sizikugwirizana kwenikweni ndi Chilamulo. Iye anati: 7 “Osangalala ndi anthu amene akhululukidwa zochita zawo zosamvera malamulo ndipo machimo awo akhululukidwa.* 8 Wosangalala ndi munthu amene Yehova* sadzawerengera tchimo lake.”+

9 Ndiye kodi anthu odulidwa okha ndi amene amakhala osangalala choncho? Kapena osadulidwa nawonso amakhala osangalala?+ Popeza timati: “Abulahamu anaonedwa kuti ndi wolungama chifukwa cha chikhulupiriro chake.”+ 10 Koma kodi iye anali wotani pamene anaonedwa kuti ndi wolungama? Kodi anali wodulidwa kapena wosadulidwa? Iyetu anali asanadulidwe. 11 Ndipo Mulungu anapatsa Abulahamu mdulidwe ngati chizindikiro+ chosonyeza kuti Mulungu anamuona kuti ndi wolungama asanadulidwe chifukwa cha chikhulupiriro. Anachita zimenezi kuti adzakhale bambo wa onse osadulidwa amene ali ndi chikhulupiriro,+ kuti anthuwo adzaonedwe kuti ndi olungama. 12 Kuti adzakhalenso bambo wa ana odulidwa, osati odulidwa okhawo, komanso wa amene amayenda moyenera potsatira chikhulupiriro chimene bambo wathu Abulahamu+ anali nacho asanadulidwe.

13 Chifukwa Abulahamu kapena mbadwa* zake sanalonjezedwe kuti adzalandira dziko monga cholowa chawo chifukwa cha Chilamulo ayi.+ Analandira lonjezolo chifukwa chakuti Abulahamu anali ndi chikhulupiriro ndipo Mulungu anamuona kuti ndi wolungama.+ 14 Chifukwa ngati anthu amene akutsatirabe Chilamulo ndi amene adzalandire cholowacho, ndiye kuti chikhulupiriro chilibenso ntchito ndipo lonjezo lija lathetsedwa. 15 Zoona zake nʼzakuti, kuphwanya Chilamulo kumachititsa kuti munthu alandire chilango,+ koma pamene palibe lamulo, palibenso kulakwa.+

16 Nʼchifukwa chake iye anapatsidwa lonjezolo chifukwa cha chikhulupiriro, kuti likhale logwirizana ndi kukoma mtima kwakukulu.+ Komanso anapatsidwa lonjezolo kuti likhale lotsimikizika kwa anthu onse omwe ndi mbadwa* zake,+ osati otsatira Chilamulo okha, komanso otsatira chikhulupiriro cha Abulahamu yemwe ndi bambo wa tonsefe.+ 17 (Zimenezi nʼzogwirizana ndi zimene Malemba amanena kuti: “Ndakusankha kuti ukhale bambo wa mitundu yambiri.”)+ Izi zinali choncho pamaso pa Mulungu amene Abulahamu ankamukhulupirira, yemwenso amaukitsa akufa ndipo amanena za zinthu zimene palibe ngati kuti zilipo. 18 Abulahamu anali ndi chiyembekezo ndiponso chikhulupiriro chakuti adzakhala bambo wa mitundu yambiri, ngakhale kuti zimenezi zinkaoneka kuti nʼzosatheka. Anakhulupirira zimenezi mogwirizana ndi zimene zinanenedwa kuti: “Umu ndi mmene mbadwa* zako zidzakhalire.”+ 19 Ndiponso, ngakhale kuti chikhulupiriro chake sichinafooke, ankaganizira za thupi lake, limene pa nthawiyo linali ngati lakufa (popeza anali ndi zaka pafupifupi 100).+ Ankadziwanso kuti Sara ndi wokalamba kwambiri ndipo sangabereke mwana.+ 20 Koma chifukwa cha lonjezo la Mulungu, chikhulupiriro chake sichinagwedezeke ndipo chikhulupiriro chakecho chinamupatsa mphamvu moti anapereka ulemerero kwa Mulungu. 21 Iye sankakayikira kuti zimene Mulungu analonjeza anali ndi mphamvu yozichita.+ 22 Choncho “Mulungu anamuona kuti ndi wolungama.”+

23 Komabe, mawu akuti “Mulungu anamuona kuti ndi wolungama” sanalembere iye yekha.+ 24 Analemberanso ifeyo. Nafenso timaonedwa kuti ndife olungama chifukwa timakhulupirira Mulungu amene anaukitsa Yesu Ambuye wathu.+ 25 Yesu anaperekedwa chifukwa cha machimo athu+ ndipo anaukitsidwa kuti tionedwe olungama.+

5 Popeza tsopano tikuonedwa kuti ndife olungama chifukwa chokhala ndi chikhulupiriro,+ tingathe kukhala pa mtendere* ndi Mulungu kudzera mwa Ambuye wathu Yesu Khristu.+ 2 Kukhulupirira Yesu kumatithandiza kuti tizitha kufika kwa Mulungu komanso tizisangalala ndi kukoma mtima kwake kwakukulu.+ Ndipo tingathe kusangalala* chifukwa tili ndi chiyembekezo cholandira ulemerero wa Mulungu. 3 Si zokhazo, koma tikhozanso kumasangalala* tikakumana ndi mavuto+ chifukwa tikudziwa kuti mavuto athu amachititsa kuti tipirire.+ 4 Kupirira kumachititsa kuti tikhale ovomerezeka kwa Mulungu+ ndipo kukhala ovomerezeka kwa Mulungu kumachititsa kuti tikhale ndi chiyembekezo.+ 5 Chiyembekezocho sichitikhumudwitsa+ chifukwa Mulungu amasonyeza kuti amatikonda pogwiritsa ntchito mzimu woyera umene amatipatsa.+

6 Pamene tinalibe mtengo wogwira,*+ Khristu anafera anthu osalambira Mulungu pa nthawi imene anakonzeratu. 7 Chifukwa nʼzovuta kuti munthu wina afere munthu wolungama. Koma mwina munthu angalimbe mtima kufera munthu wabwino. 8 Koma Mulungu akutisonyeza chikondi chake, chifukwa pamene tinali ochimwa, Khristu anatifera.+ 9 Ndiponso adzachita zoposa pamenepo potipulumutsa ku mkwiyo wake kudzera mwa Khristu,+ popeza tikuonedwa olungama chifukwa cha magazi a Khristuyo.+ 10 Ngati tinagwirizanitsidwa ndi Mulungu kudzera mu imfa ya Mwana wake+ pa nthawi imene tinali adani, ndiye kuti tidzapulumutsidwa ndithu ndi moyo wake, popeza panopa tagwirizanitsidwa. 11 Ndipo si zokhazo, koma tikusangalalanso chifukwa cha ubwenzi wathu ndi Mulungu kudzera mwa Ambuye wathu Yesu Khristu, amene tagwirizanitsidwa ndi Mulungu kudzera mwa iye.+

12 Uchimo unalowa mʼdziko kudzera mwa munthu mmodzi ndipo uchimowo unabweretsa imfa.+ Choncho imfayo inafalikira kwa anthu onse chifukwa onse anachimwa . . .+ 13 Chilamulo chisanabwere, uchimo unalipo kale mʼdziko, koma munthu sangapezedwe ndi mlandu woti wachita tchimo ngati palibe lamulo.+ 14 Ngakhale zili choncho, imfa inalamulira ngati mfumu kuyambira nthawi ya Adamu mpaka ya Mose, ngakhalenso kwa anthu amene sanachimwe ngati mmene anachimwira Adamu, yemwe ndi wofanana ndi amene ankabwera.+

15 Koma mmene zilili ndi mphatsoyi, si mmene zinalili ndi uchimowo. Anthu ambiri anafa chifukwa cha uchimo wa munthu mmodzi. Koma kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu ndiponso mphatso yake yaulere imene anaipereka mokoma mtima kudzera mwa munthu mmodzi,+ Yesu Khristu, nʼzapamwamba kwambiri. Pogwiritsa ntchito mphatso imeneyi, Mulungu adzapereka madalitso osaneneka kwa anthu ambiri.+ 16 Pali kusiyananso pakati pa mphatso yaulereyi ndi mmene zinthu zinachitikira kudzera mwa munthu mmodzi amene anachimwa.+ Chiweruzo cha tchimo limodzi lija chinabweretsa uchimo kwa onse,+ koma mphatso imene inaperekedwa chifukwa cha machimo ambiri, inachititsa kuti anthu azionedwa kuti ndi olungama.+ 17 Imfa inalamulira ngati mfumu chifukwa cha uchimo wa munthu mmodziyo.+ Koma anthu amene alandira kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu ndiponso mphatso yake yaulere ya chilungamo,+ adzakhala ndi moyo kuti alamulire ngati mafumu+ kudzera mwa munthu mmodziyu, Yesu Khristu.+

18 Choncho, mmene zinakhalira kuti uchimo umodzi unachititsa kuti anthu osiyanasiyana aweruzidwe kuti ndi ochimwa,+ kuchita chinthu chimodzi cholungama kwachititsanso kuti anthu osiyanasiyana+ aonedwe kuti ndi olungama kuti akhale ndi moyo.+ 19 Popeza kusamvera kwa munthu mmodziyo kunachititsa kuti ambiri akhale ochimwa,+ kumvera kwa munthu mmodziyu kudzachititsanso kuti ambiri akhale olungama.+ 20 Chilamulo chinaperekedwa kuti kuchimwa kwa anthu kuonekere.+ Koma pamene uchimo unaonekera, kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu kunawonjezekanso kwambiri. 21 Chifukwa chiyani? Kuti mmene uchimo unalamulira ngati mfumu pamodzi ndi imfa,+ nakonso kukoma mtima kwakukulu kulamulire ngati mfumu kudzera mʼchilungamo. Ndipo zimenezi zidzachititsa kuti anthu apeze moyo wosatha kudzera mwa Yesu Khristu Ambuye wathu.+

6 Ndiye tinene kuti chiyani? Kodi tipitirize kuchimwa kuti kukoma mtima kwakukulu kuwonjezeke? 2 Ayi ndithu. Popeza tinafa ku uchimo,+ ndiye tipitirize kuchimwa chifukwa chiyani?+ 3 Kapena simudziwa kuti tonsefe amene tinabatizidwa ndipo tsopano ndife ogwirizana ndi Khristu Yesu+ tinabatizidwanso mu imfa yake?+ 4 Choncho tinaikidwa naye limodzi mʼmanda pamene tinabatizidwa mu imfa yake,+ kuti mofanana ndi Khristu amene anaukitsidwa kudzera mu ulemerero wa Atate, ifenso tikhale moyo watsopano.+ 5 Chifukwa ngati tagwirizana naye pofa imfa yofanana ndi yake,+ ndithudi tidzagwirizananso naye poukitsidwa mofanana naye.+ 6 Chifukwa tikudziwa kuti umunthu wathu wakale unapachikidwa naye+ limodzi pamtengo nʼcholinga chakuti thupi lathu lauchimo likhale lopanda mphamvu,+ kuti tisakhalenso akapolo a uchimo.+ 7 Chifukwa munthu amene wafa sakhalanso ndi mlandu* wa machimo ake.

8 Ndiponso, ngati tinafa limodzi ndi Khristu, timakhulupirira kuti tidzakhalanso ndi moyo limodzi ndi iye. 9 Tikudziwa kuti popeza Khristu waukitsidwa,+ sadzafanso+ ndipo imfa sikumulamuliranso ngati mfumu. 10 Iye anafa kuti achotse uchimo kamodzi kokha basi+ ndipo moyo umene ali nawo, ali nawo kuti azichita chifuniro cha Mulungu. 11 Nanunso muzidziona ngati akufa pa nkhani ya uchimo, koma amoyo kwa Mulungu mwa Khristu Yesu.+

12 Choncho musalole kuti uchimo uzilamulirabe ngati mfumu mʼmatupi anu oti akhoza kufawo+ kuti muzitsatira zilakolako zawo. 13 Ndipo musapereke matupi* anu ku uchimo kuti akhale zida zochitira zinthu zosalungama, koma dziperekeni kwa Mulungu ngati anthu amene aukitsidwa. Matupi anunso muwapereke kwa Mulungu ngati zida zochitira chilungamo.+ 14 Uchimo usamakulamulireni ngati mfumu, chifukwa simukutsatira Chilamulo,+ koma mukusangalala ndi kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu.+

15 Kodi zikatere ndiye kuti tizichita tchimo chifukwa chakuti sitikutsatira Chilamulo koma tikusangalala ndi kukoma mtima kwakukulu?+ Ayi ndithu. 16 Kodi simukudziwa kuti mukamadzipereka kwa winawake ngati akapolo omvera, mumakhala akapolo a amene mukumumverayo?+ Mumakhala akapolo a uchimo+ umene umatsogolera ku imfa,+ kapena akapolo a kumvera komwe kumatsogolera ku chilungamo. 17 Koma tikuthokoza Mulungu kuti ngakhale kuti poyamba munali akapolo a uchimo, munamvera mochokera pansi pa mtima mfundo zatsopano zomwe munaphunzitsidwa. 18 Inde, popeza munamasulidwa ku uchimo,+ munakhala akapolo a chilungamo.+ 19 Ndikulankhulatu ngati munthu chifukwa cha kufooka kwa matupi anu. Mmene munaperekera ziwalo zanu kuti zikhale akapolo a zonyansa ndiponso akapolo a kusamvera malamulo nʼcholinga chakuti muzichita zinthu zophwanya malamulo, perekaninso ziwalo zanu kuti mukhale akapolo a chilungamo ndiponso oyera.+ 20 Chifukwa pamene munali akapolo a uchimo, munali omasuka ku chilungamo.

21 Kodi pa nthawiyo munkabala zipatso zotani? Zinali zinthu zimene panopa mumachita nazo manyazi. Ndipo mapeto a zinthu zimenezo ndi imfa.+ 22 Koma tsopano chifukwa munamasulidwa ku uchimo nʼkukhala akapolo a Mulungu, mukubala zipatso za chiyero+ ndipo pamapeto pake mudzakhala ndi moyo wosatha.+ 23 Chifukwa malipiro a uchimo ndi imfa,+ koma mphatso imene Mulungu amapereka ndi moyo wosatha+ kudzera mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.+

7 Ndikulankhula ndi inu abale, amene mumadziwa Chilamulo. Kodi simukudziwa kuti Chilamulo chimakhala ndi mphamvu pa munthu pamene munthuyo ali ndi moyo? 2 Mwachitsanzo, mkazi wokwatiwa amakhala womangidwa kwa mwamuna wake mwalamulo pamene mwamunayo ali moyo. Koma mwamunayo akamwalira, mkazi amakhala womasuka ku lamulo lokhudza mwamuna wake.+ 3 Ngati mkaziyo angakwatiwe ndi mwamuna wina mwamuna wake ali moyo, ndiye kuti wachita chigololo.+ Koma ngati mwamuna wake wamwalira, mkaziyo wamasuka ku lamulo lokhudza mwamuna wake, choncho sanachite chigololo ngati atakwatiwa ndi mwamuna wina.+

4 Abale anga, thupi la Khristu linakumasulani ku Chilamulo, kuti mukhale a winawake+ amene anaukitsidwa+ nʼcholinga choti tibale zipatso kwa Mulungu.+ 5 Chifukwa pamene tinkakhala mogwirizana ndi matupi athu ochimwawa, Chilamulo chinachititsa kuti zilakolako za uchimo zimene tinali nazo mʼmatupi* mwathu zionekere. Ndipo zilakolako zimenezi zikanatibweretsera imfa.+ 6 Koma tsopano tamasulidwa ku Chilamulo,+ chifukwa tafa ku Chilamulo chimene chinkatimanga, kuti tikhale akapolo mʼnjira yatsopano motsogoleredwa ndi mzimu,+ osati mʼnjira yakale motsogoleredwa ndi malamulo olembedwa.+

7 Ndiye tinene kuti chiyani? Kodi Chilamulo ndi uchimo? Ayi ndithu. Kunena zoona, sindikanadziwa uchimo zikanakhala kuti panalibe Chilamulo.+ Mwachitsanzo, sindikanadziwa kusirira kwa nsanje zikanakhala kuti Chilamulo sichinanene kuti: “Usasirire mwansanje.”+ 8 Koma chifukwa cha lamulo, uchimo unapeza njira yondichititsa kukhala ndi kusirira kwansanje kwa mtundu uliwonse. Chifukwa popanda Chilamulo, uchimo unali wopanda mphamvu.*+ 9 Chilamulo chisanaperekedwe ndinali wamoyo. Koma Chilamulo chitafika, uchimo unakhalanso ndi moyo, koma ineyo ndinafa.+ 10 Ndipo lamulo limene linkafunika kunditsogolera kuti ndipeze moyo,+ linanditsogolera ku imfa. 11 Uchimo unagwiritsa ntchito lamulo limeneli pondinyengerera ndipo unandipha. 12 Choncho Chilamulo pachokha nʼchoyera ndipo malamulo ndi oyera, olungama ndiponso abwino.+

13 Kodi zimenezi zikutanthauza kuti chinthu chabwino chinachititsa kuti ndife? Ayi. Uchimo ndi umene unachititsa kuti ndife. Chilamulo nʼchabwino, kungoti chinachititsa kuti zidziwike bwino kuti uchimo ukuchititsa kuti ndife.+ Choncho malamulo anatithandiza kudziwa kuti uchimo ndi woipa kwambiri.+ 14 Chifukwa tikudziwa kuti Chilamulo nʼchochokera kwa Mulungu kudzera mwa mzimu, koma ineyo si ine wangwiro ndipo ndinagulitsidwa ku uchimo.+ 15 Sinditha kumvetsa zimene zimandichitikira. Chifukwa zimene ndimafuna kuchita, sindizichita. Koma zimene ndimadana nazo nʼzimene ndimachita. 16 Komabe ngati ndimachita zimene sindikufuna kuchita, ndiye kuti ndikuvomereza kuti Chilamulo nʼchabwino. 17 Komano amene akuchita zimenezo si inenso, koma uchimo umene uli ndi ine.+ 18 Ndikudziwa kuti mʼthupi langa lochimwali, mulibe chilichonse chabwino. Chifukwa ndimafuna kuchita zabwino, koma sinditha kuzichita.+ 19 Zinthu zabwino zimene ndimafuna kuchita sindichita, koma zoipa zimene sindifuna kuchita nʼzimene ndimachita. 20 Tsopano ngati ndimachita zimene sindifuna ndiye kuti amene ndikuchita zimenezo si inenso, koma uchimo umene uli ndi ine.

21 Zimene zimandichitikira ndi zakuti,* pamene ndikufuna kuchita zinthu zabwino, zoipa zimakhala mkati mwangamu.+ 22 Mumtima mwanga ndimasangalala kwambiri ndi malamulo a Mulungu,+ 23 koma ndimaona lamulo lina mʼthupi* langa likumenyana ndi malamulo amʼmaganizo mwanga+ nʼkundichititsa kukhala kapolo wa lamulo la uchimo+ limene lili mʼthupi* langa. 24 Munthu womvetsa chisoni ine! Ndani adzandipulumutse ku thupi limene likundichititsa kuti ndifeli? 25 Mulungu adzandipulumutsa kudzera mwa Yesu Khristu Ambuye wathu. Choncho mʼmaganizo mwanga ndine kapolo wa malamulo a Mulungu, koma mʼthupi langa ndine kapolo wa lamulo la uchimo.+

8 Choncho anthu amene ali ogwirizana ndi Khristu Yesu alibe mlandu. 2 Chifukwa lamulo la mzimu limene limapatsa moyo mogwirizana ndi Khristu Yesu lakumasulani+ ku lamulo la uchimo ndi la imfa. 3 Chilamulo chinalibe mphamvu yokumasulani+ chifukwa anthu ndi ofooka+ komanso ochimwa. Koma kuti akumasuleni, Mulungu anatumiza Mwana wake+ ali ndi thupi ngati la anthu ochimwa+ kuti athane ndi uchimo. Choncho Mulungu anagonjetsa uchimo pogwiritsa ntchito thupi. 4 Mulungu anachita izi kuti ife amene timayenda motsatira mzimu, osati motsatira zofuna za thupi,+ tikwaniritse zinthu zolungama zimene Chilamulo chimafuna.+ 5 Chifukwa otsatira zofuna za thupi, maganizo awo onse amakhala pa zinthu za thupi.+ Koma otsatira mzimu, maganizo awo onse amakhala pa zinthu za mzimu.+ 6 Popeza kuganizira kwambiri zinthu za thupi kumabweretsa imfa,+ koma kuganizira kwambiri zinthu za mzimu kumabweretsa moyo ndi mtendere.+ 7 Chifukwa kuganizira kwambiri zinthu za thupi kumayambitsa udani ndi Mulungu+ popeza thupi siligonjera lamulo la Mulungu, ndipotu kunena zoona, silingaligonjere. 8 Choncho amene amatsatira zofuna za thupi sangakondweretse Mulungu.

9 Komabe inu mukutsatira mzimu osati zofuna za thupi,+ ngati mzimu wa Mulungu ulidi ndi inu. Ngati wina alibe mzimu wa Khristu, ameneyu si wa Khristu. 10 Koma ngati muli ogwirizana ndi Khristu,+ mzimu umachititsa kuti mukhale ndi moyo chifukwa cha chilungamo ngakhale kuti thupi ndi lakufa chifukwa cha uchimo. 11 Ngati mzimu wa amene anaukitsa Yesu uli ndi inu, iye amene anaukitsa Khristu Yesu adzachititsanso matupi anu omwe angathe kufawo+ kukhala ndi moyo,+ pogwiritsa ntchito mzimu wake umene uli ndi inu.

12 Choncho abale, tili ndi ngongole, osati ndi thupi kuti tizikhala motsatira zofuna za thupi.+ 13 Chifukwa ngati mukukhala motsatira zofuna za thupi, ndiye kuti mosakayikira mudzafa.+ Koma mukalola kuti mphamvu ya mzimu ikuthandizeni kupha zochita za thupi, mudzakhala ndi moyo.+ 14 Onse amene akutsogoleredwa ndi mzimu wa Mulungu, ndi anadi a Mulungu.+ 15 Chifukwa simunalandire mzimu wa ukapolo woyambitsanso mantha, koma munalandira mzimu wakuti mukhale ana, umene timafuula nawo kuti: “Abba,* Atate!”+ 16 Mzimuwo umachitira umboni limodzi ndi mzimu wathu+ kuti ndife ana a Mulungu.+ 17 Choncho ngati tili ana, ndifenso olandira cholowa kuchokera kwa Mulungu. Koma ndifenso olandira cholowa+ anzake a Khristu, ngati tikuvutika naye limodzi+ kuti tikalandire naye ulemerero.+

18 Ndikuona kuti mavuto amene tikukumana nawo panopa ndi aangʼono powayerekezera ndi ulemerero umene udzaonekere kudzera mwa ife.+ 19 Chifukwa chilengedwe chikuyembekezera mwachidwi nthawi imene ulemerero wa ana a Mulungu udzaonekere.+ 20 Popeza chilengedwe chinaweruzidwa kuti chikhale chopanda pake,+ osati mwa kufuna kwake koma kudzera mwa amene anachiweruza. Ndipo anaperekanso chiyembekezo 21 chakuti chilengedwecho chidzamasulidwa+ ku ukapolo wa thupi limene limawonongeka nʼkukhala ndi ufulu waulemerero wa ana a Mulungu. 22 Chifukwa tikudziwa kuti chilengedwe chonse chikubuula pamodzi komanso kumva kuwawa pamodzi mpaka pano. 23 Komatu si zokhazi. Ifeyo amene tili ndi zipatso zoyambirira zomwe ndi mzimu, tikubuula mumtima mwathu+ pamene tikudikira ndi mtima wonse kuti Mulungu atitenge kukhala ana ake,+ kutimasula ndi dipo* ku matupi athuwa. 24 Chifukwa tinapulumutsidwa tili ndi chiyembekezo chimenechi, koma chimene ukuchiyembekezera chikatheka sichikhalanso chiyembekezo. Kodi chimene munthu ankachiyembekezera chikachitika, amachiyembekezerabe? 25 Koma ngati zimene tikuyembekezera+ sizinachitike,+ timadikirabe mopirira.+

26 Mofanana ndi zimenezi, mzimu umatithandiza pa zimene tikulephera kuchita.+ Chifukwa vuto ndi lakuti sitidziwa zimene tikufunika kutchula popemphera, koma mzimu umachonderera mʼmalo mwathu ndi madandaulo amene sitinathe kuwafotokoza. 27 Koma iye amene amafufuza mitima+ amadziwa zimene mzimu ukutanthauza, chifukwa umachonderera mʼmalo mwa oyera mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu.

28 Tikudziwa tsopano kuti Mulungu amagwirizanitsa zochita zake zonse pofuna kuthandiza amene amakonda Mulunguyo, anthu oitanidwa mogwirizana ndi cholinga chake.+ 29 Amatero chifukwa amene anawadziwa choyamba anawasankhiratu kuti adzakhale ofanana ndi Mwana wake,+ kuti iye akhale woyamba kubadwa+ pakati pa abale ake ambiri.+ 30 Ndiponso amene anawasankhiratu+ ndi amene anawaitana.+ Amene anawaitanawo ndi amenenso amawaona kuti ndi olungama.+ Ndipo amene amawaona kuti ndi olungamawo ndi amenenso anawapatsa ulemerero.+

31 Ndiye tinene kuti chiyani pamenepa? Ngati Mulungu ali kumbali yathu, ndani adzatsutsana nafe?+ 32 Popeza sanaumire ngakhale Mwana wake koma anamupereka mʼmalo mwa ife tonse,+ angalephere bwanji kutipatsanso mokoma mtima zinthu zina zonse pamodzi ndi Mwana wakeyo? 33 Ndani adzasumira mlandu anthu a Mulungu ochita kusankhidwa?+ Popeza Mulungu ndi amene amawaona kuti ndi olungama,+ 34 ndani adzawatsutsa? Khristu Yesu ndi amene anafa komanso ndi amene anaukitsidwa. Iye ali kudzanja lamanja la Mulungu,+ ndipo amatilankhulira mochonderera.+

35 Ndani adzatisiyanitsa ndi chikondi cha Khristu?+ Kodi ndi masautso, zowawa, kuzunzidwa, njala, usiwa, zoopsa kapena lupanga?+ 36 Malemba amati: “Chifukwa cha inu, tikuphedwa nthawi zonse. Takhala ngati nkhosa zokaphedwa.”+ 37 Koma tikugonjetsa zinthu zonsezi+ mothandizidwa ndi iye amene anatikonda. 38 Chifukwa ndatsimikiza mtima kuti imfa, moyo, angelo, maboma, zinthu zimene zilipo, zinthu zimene zikubwera, mphamvu,+ 39 msinkhu, kuzama kapena cholengedwa chilichonse, sizidzatha kutisiyanitsa ndi chikondi cha Mulungu chimene chili mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.

9 Ndikunena zoona mogwirizana ndi Khristu, sindikunama ayi. Ndipo chikumbumtima changa chikundichitira umboni mwa mzimu woyera, 2 kuti ndikumva chisoni kwambiri ndipo mtima umandipweteka nthawi zonse. 3 Ndikanakonda kuti ineyo ndisiyanitsidwe ndi Khristu ngati wotembereredwa mʼmalo mwa abale anga, anthu a mtundu wanga, 4 omwe ndi Aisiraeli. Mulungu anawatenga kuti akhale ana ake+ ndipo anawapatsa ulemerero, mapangano,+ Chilamulo,+ utumiki wopatulika+ komanso malonjezo.+ 5 Iwo ndi ana a makolo athu akale.+ Komanso Khristu anabadwa ngati munthu kuchokera kwa iwo.+ Mulungu, yemwe ndi wamkulu pa zinthu zonse, atamandike mpaka kalekale. Ame.

6 Komabe sizikutanthauza kuti mawu a Mulungu sanakwaniritsidwe. Chifukwa si onse omwe ndi mbadwa za Aisiraeli amene alidi “Aisiraeli.”+ 7 Ndiponso sikuti onse ndi ana chifukwa choti ndi mbadwa* za Abulahamu.+ Koma Malemba amati, “Mbadwa* zimene ndinakulonjeza zidzachokera mwa Isaki.”+ 8 Izi zikutanthauza kuti si ana akuthupi amene alidi ana a Mulungu,+ koma ana obadwa mogwirizana ndi lonjezo+ ndi amene amatengedwa kuti ndi mbadwa.* 9 Popeza lonjezo lija linati: “Ndidzabweranso nthawi ngati yomwe ino, ndipo Sara adzakhala ndi mwana wamwamuna.”+ 10 Lonjezolo silinaperekedwe pa nthawi iyi yokha. Linaperekedwanso pamene Rabeka ankayembekezera kubereka ana amapasa a Isaki kholo lathu lija.+ 11 Mapasawo asanabadwe ndiponso asanachite chabwino kapena choipa chilichonse, Mulungu anasonyeza kuti cholinga chake chidzadalira iye amene amaitana, osati zochita za munthu. 12 Choncho anauza Rabeka kuti: “Wamkulu adzakhala kapolo wa wamngʼono.”+ 13 Mogwirizana ndi zimene Malemba amanena kuti: “Ndinakonda Yakobo, koma Esau ndinadana naye.”+

14 Ndiye tinene kuti chiyani pamenepa? Kodi Mulungu alibe chilungamo? Ayi ndithu.+ 15 Chifukwa iye anauza Mose kuti: “Amene ndikufuna kumukomera mtima ndidzamukomera mtima, ndipo amene ndikufuna kumusonyeza chifundo, ndidzamusonyeza chifundo.”+ 16 Choncho sizidalira kufuna kwa munthu kapena khama lake,* koma Mulungu amene ndi wachifundo.+ 17 Ponena za Farao, lemba lina linati: “Ndakusiya ndi moyo kuti ndikusonyeze mphamvu zanga komanso kuti dzina langa lilengezedwe padziko lonse lapansi.”+ 18 Choncho iye amachitira chifundo munthu amene wafuna kumuchitira chifundo, koma amalola anthu ena kuti aumitse mitima yawo.+

19 Mwina ungandiuze kuti: “Nʼchifukwa chiyani Mulungu akupezerabe anthu zifukwa? Kodi ndani akutsutsa chifuniro chake?” 20 Munthu iwe, ndiwe ndani kuti uziyankhana ndi Mulungu?+ Kodi chinthu choumbidwa chingauze munthu amene anachiumba kuti, “Unandipangiranji chonchi?”+ 21 Kodi simukudziwa kuti woumba mbiya ali ndi ufulu woumba+ chinthu china cha ntchito yolemekezeka, china cha ntchito yonyozeka kuchokera pa dongo limodzi? 22 Ndiye bwanji ngati Mulungu anafuna kusonyeza mkwiyo wake kuti mphamvu zake zidziwike ndipo analekerera moleza mtima kwambiri anthu oyenera kuwonongedwa amene anamukwiyitsa?* 23 Ndiponso bwanji ngati anachita zimenezo kuti asonyeze kukula kwa ulemerero wake kwa anthu oyenera kuwachitira chifundo,*+ omwe anawakonzeratu kuti alandire ulemerero, 24 ndipo anthu ake ndi ifeyo amene anatiitana osati kuchokera kwa Ayuda okha komanso ku mitundu ina?+ 25 Ndi zofanananso ndi zimene ananena mʼbuku la Hoseya kuti: “Anthu amene si anthu anga+ ndidzawatchula kuti ‘anthu anga,’ ndipo mkazi amene sankakondedwa ndidzamutchula kuti ‘wokondedwa.’+ 26 Kumene ankauzidwa kuti, ‘Siinu anthu anga,’ adzauzidwa kuti, ‘Ndinu ana a Mulungu wamoyo.’”+

27 Komanso, Yesaya analengeza zokhudza Isiraeli kuti: “Ngakhale kuti ana a Isiraeli adzakhala ambiri ngati mchenga wakunyanja, ochepa okha ndi amene adzapulumuke.+ 28 Chifukwa Yehova* adzaweruza milandu padziko lapansi nʼkuimaliza mwamsanga.”+ 29 Ndiponso mogwirizana ndi zimene Yesaya ananeneratu, “Yehova* wa magulu ankhondo akumwamba akanapanda kutisiyira mbadwa,* tikanakhala ngati Sodomu, ndipo tikanafanana ndi Gomora.”+

30 Ndiye pamenepa tinene kuti chiyani? Ngakhale kuti anthu a mitundu ina sanatsatire chilungamo,+ iwo anapeza chilungamo chimene chimabwera chifukwa cha chikhulupiriro.+ 31 Koma ngakhale kuti Aisiraeli ankatsatira lamulo la chilungamo, sanakwanitse kutsatira lamulolo. 32 Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti ankaganiza kuti angalitsatire mʼzochita zawo, osati mwa chikhulupiriro. Iwo anapunthwa “pamwala wopunthwitsa”+ 33 mogwirizana ndi zimene Malemba amanena kuti: “Inetu ndikuika mwala+ wopunthwitsa ndiponso thanthwe lokhumudwitsa mu Ziyoni, koma munthu wokhulupirira mwalawo sadzakhumudwa.”+

10 Abale, chimene ndikufunitsitsa mumtima mwanga ndiponso pemphero langa lochonderera kwa Mulungu ndi lakuti anthu a mtundu wanga apulumutsidwe.+ 2 Chifukwa ndikuwachitira umboni kuti ndi odzipereka potumikira Mulungu,+ koma sakumudziwa molondola. 3 Ndipo chifukwa chosadziwa chilungamo cha Mulungu,+ iwo sanagonjere chilungamocho+ koma anafuna kukhazikitsa chawochawo.+ 4 Khristu ndiye kutha kwa Chilamulo,+ kuti aliyense wokhulupirira akhale wolungama.+

5 Pajatu Mose analemba zokhudza mmene munthu angachitire chilungamo mogwirizana ndi Chilamulo, anati: “Aliyense amene akuchita zimenezi adzakhala ndi moyo chifukwa cha malamulo.”+ 6 Koma za chilungamo chimene chimabwera chifukwa cha chikhulupiriro, Malemba amati: “Mumtima mwako usanene kuti,+ ‘Kodi ndani adzapite kumwamba?’+ kuti akatsitse Khristu. 7 Kapena, ‘Kodi ndani adzapite kuphompho?’+ kuti akaukitse Khristu.” 8 Koma kodi lemba limati chiyani? Limati: “Mawu a chilamulowo ali pafupi ndi inu, ali mʼkamwa mwanu ndi mumtima mwanu,”+ amenewa ndi “mawu” a chikhulupiriro amene tikulalikira. 9 Chifukwa ngati ukulengeza ‘mawu amene ali mʼkamwa mwakowo,’ akuti Yesu ndi Ambuye,+ ndipo mumtima mwako ukukhulupirira kuti Mulungu anamuukitsa, udzapulumuka. 10 Kuti munthu akhale wolungama amayenera kukhala ndi chikhulupiriro mumtima mwake, koma ndi pakamwa pake amalengeza+ poyera chikhulupiriro chake kuti apulumuke.

11 Paja lemba lina limati: “Palibe wokhulupirira iye amene adzakhumudwe.”+ 12 Palibe kusiyana pakati pa Myuda ndi Mgiriki,+ popeza kwa onsewo Ambuye ndi mmodzi, amene amapereka mowolowa manja kwa onse oitana pa dzina lake. 13 Chifukwa “aliyense woitana pa dzina la Yehova* adzapulumuka.”+ 14 Komabe, kodi angaitane bwanji pa dzina lake ngati samukhulupirira? Angakhulupirire bwanji ngati sanamvepo za iye? Nanga angamve bwanji za iye popanda wina kulalikira? 15 Ndipo angalalikire bwanji ngati sanatumidwe?+ Zili ngati mmene Malemba amanenera kuti: “Mapazi a anthu olengeza uthenga wabwino wa zinthu zabwino, ndi okongola kwambiri.”+

16 Ngakhale zili choncho, si onse amene anatsatira uthenga wabwino. Chifukwa Yesaya anati: “Yehova,* kodi ndani wakhulupirira zimene anamva kwa ife?”+ 17 Choncho munthu amakhala ndi chikhulupiriro chifukwa cha zimene wamva.+ Ndipo zimene wamvazo zimachokera mʼmawu onena za Khristu. 18 Koma ndifunse kuti, Kodi kumva sanamve? Pajatu “mawu awo anamveka padziko lonse lapansi, ndipo uthenga wawo unamveka mpaka kumalekezero a dziko lapansi kumene kuli anthu.”+ 19 Komanso ndifunse kuti, Kodi si zoona kuti Aisiraeli anadziwa?+ Choyamba Mose anati: “Ndidzakuchititsani nsanje pogwiritsa ntchito anthu omwe si Aisiraeli. Ndidzakukwiyitsani koopsa pogwiritsa ntchito mtundu wopusa.”+ 20 Koma Yesaya analankhula molimba mtima kwambiri kuti: “Anthu amene anandipeza ndi amene sankandifunafuna.+ Ndinadziwika kwa anthu amene sanafunse za ine.”+ 21 Koma ponena za Aisiraeli iye anati: “Ndatambasula manja anga tsiku lonse kwa anthu osamvera ndiponso amakani.”+

11 Ndiye ndifunse kuti, kodi Mulungu anakana anthu ake?+ Ayi ndithu. Paja inenso ndine mmodzi wa Aisiraeli, mbadwa* ya Abulahamu, wa fuko la Benjamini. 2 Mulungu sanakane anthu ake amene anali oyambirira kuwavomereza.+ Kodi simukudziwa zimene lemba lina limanena zokhudza Eliya, pamene anachonderera Mulungu motsutsa Aisiraeli? Limati: 3 “Yehova,* iwo apha aneneri anu ndipo agwetsa maguwa anu ansembe moti ine ndatsala ndekhandekha. Tsopano ayambanso kundifunafuna kuti andiphe.”+ 4 Koma kodi Mulungu anamuuza kuti chiyani? Anamuuza kuti: “Ine ndasiya anthu 7,000 amene mawondo awo sanagwadirepo Baala.”+ 5 Choncho, pa nthawi inonso alipo ena ochepa amene anasankhidwa+ mwa kukoma mtima kwakukulu. 6 Ndiyetu ngati anasankhidwa mwa kukoma mtima kwakukulu,+ sanasankhidwe chifukwa cha ntchito zawo ayi.+ Zitati zitero, kukoma mtima kumeneko sikungakhalenso kukoma mtima kwakukulu.

7 Ndiye zili bwanji pamenepa? Chimene Aisiraeli akuchifunitsitsa sanachipeze, koma anthu osankhidwa ndi amene anachipeza.+ Enawo anaumitsa mitima yawo+ 8 ngati mmene Malemba amanenera kuti: “Mulungu wawapatsa mzimu wa tulo tofa nato,+ maso osaona ndi makutu osamva, mpaka lero.”+ 9 Ndiponso Davide anati: “Tebulo lawo likhale khwekhwe, msampha, chopunthwitsa ndi chilango kwa iwo. 10 Maso awo achite mdima kuti asaone, ndipo weramitsani misana yawo nthawi zonse.”+

11 Ndiyeno ndifunse kuti, kodi anapunthwa mpaka kugweratu? Ayi. Koma chifukwa cha kulakwa kwawo anthu a mitundu ina apeza chipulumutso, ndipo zimenezi zachititsa kuti olakwawo achite nsanje.+ 12 Kulakwa kwawo kwabweretsa chuma mʼdziko ndipo kuchepa kwawo kukutanthauza chuma kwa anthu a mitundu ina.+ Choncho padzakhala madalitso ambiri chiwerengero chawo chikadzakwanira.

13 Tsopano ndikulankhula ndi inu anthu a mitundu ina. Popeza ndine mtumwi wotumidwa kwa anthu a mitundu ina,+ ndimalemekeza utumiki wanga,+ 14 kuti mwina ndingapangitse anthu a mtundu wanga kuchita nsanje nʼkupulumutsapo ena a iwo. 15 Chifukwatu ngati dziko lagwirizanitsidwa ndi Mulungu chifukwa chakuti iwo anatayidwa,+ ndiye kuti akadzalandiridwa zidzakhala ngati awaukitsa. 16 Ndiponso, ngati mbali ya mtanda wa mkate imene yaperekedwa nsembe ngati chipatso choyambirira ili yoyera, ndiye kuti mtanda wonse ndi woyeranso. Ndipo ngati muzu uli woyera, ndiye kuti nthambinso ndi zoyera.

17 Ngati nthambi zina zinadulidwa, ndipo iwe ngakhale kuti ndiwe nthambi ya mtengo wa maolivi wamʼtchire, unalumikizidwa pakati pa nthambi zotsala ndipo unayamba kupeza zonse zofunika kuchokera ku muzu wamtengo wa maoliviwo, 18 usayambe kukulira mtima nthambi zimene zinadulidwazo. Koma ngati ukuzikulira mtima+ kumbukira kuti si iwe amene ukunyamula muzu, koma muzu ndi umene ukukunyamula iweyo. 19 Mwina ukunena kuti: “Anadula nthambi zina kuti alumikizepo ineyo.”+ 20 Zimenezo nʼzoona. Iwo anadulidwa chifukwa analibe chikhulupiriro,+ koma iweyo udakali wolumikizidwa kumtengowo chifukwa cha chikhulupiriro.+ Chotsa maganizo odzikuzawo, koma khala ndi mantha. 21 Chifukwa ngati Mulungu sanalekerere nthambi zachilengedwe, sadzakulekereranso iweyo. 22 Uziganizira kukoma mtima komanso kusalekerera kwa Mulungu.+ Amene anagwa anasonyezedwa kusalekerera,+ koma iweyo unasonyezedwa kukoma mtima kwa Mulungu. Bola ukhalebe woyenera kusonyezedwa kukoma mtima kwake. Apo ayi, iwenso udzadulidwa. 23 Iwonso ngati angayambe kukhala ndi chikhulupiriro, adzalumikizidwa kumtengowo,+ chifukwa Mulungu akhoza kuwalumikizanso. 24 Ngati iweyo unadulidwa kumtengo wa maolivi umene mwachilengedwe umamera mʼtchire, ndipo mosemphana ndi chilengedwe unalumikizidwa kumtengo wa maolivi wolimidwa, kodi si chapafupi kulumikiza nthambizi kumtengo wawo umene zinadulidwako?

25 Chifukwa sindikufuna kuti mukhale osadziwa abale za chinsinsi chopatulika chimenechi,+ kuopera kuti mungadzione ngati anzeru. Chinsinsicho nʼchakuti ena mu Isiraeli aumitsa mitima yawo mpaka chiwerengero chonse cha anthu ochokera mʼmitundu ina chitakwanira. 26 Aisiraeli onse adzapulumutsidwa mwa njira imeneyi+ mogwirizana ndi zimene Malemba amanena kuti: “Mpulumutsi adzachokera mʼZiyoni+ ndipo adzachotsera Yakobo zochita zonse zosalemekeza Mulungu. 27 Limeneli ndi pangano limene ndidzachite nawo+ ndikadzawachotsera machimo awo.”+ 28 Nʼzoona kuti iwo ndi adani a uthenga wabwino ndipo zimenezi zakuthandizani inuyo. Koma Mulungu anawasankha ndipo amawakonda chifukwa cha makolo awo akale.+ 29 Mulungu sadzanongʼoneza bondo chifukwa cha mphatso zake ndiponso chifukwa chakuti anawaitana. 30 Inuyo munali osamvera Mulungu,+ koma tsopano mwasonyezedwa chifundo+ chifukwa cha kusamvera kwawo.+ 31 Iwowa tsopano ndi osamvera ndipo Mulungu wakusonyezani chifundo. Koma akhoza kuwasonyezanso chifundo ngati mmene anachitira ndi inuyo. 32 Mulungu walola onse kuti akhale akaidi a kusamvera+ kuti onsewo awasonyeze chifundo.+

33 Ndithudi, madalitso amene Mulungu amapereka ndi ochuluka kwambiri. Nzeru zake nʼzozama, ndiponso iye ndi wodziwa zinthu kwambiri. Ziweruzo zake ndi zovuta kuzimvetsa, ndipo ndani angatulukire njira zake? 34 “Ndani akudziwa maganizo a Yehova,* kapena ndani angakhale mlangizi wake?”+ 35 Kapenanso “ndani anayambirira kumupatsa kanthu, kuti amubwezere?”+ 36 Chifukwa zinthu zonse zimachokera kwa iye, ndi iyeyo amene anazipanga ndiponso ndi zake. Ulemerero ukhale wake mpaka kalekale. Ame.

12 Choncho abale, ndikukudandaulirani mwa chifundo chachikulu cha Mulungu kuti mupereke matupi anu+ ngati nsembe yamoyo, yoyera+ ndiponso yovomerezeka kwa Mulungu, yomwe ndi utumiki wopatulika pogwiritsa ntchito luso la kuganiza.+ 2 Musamatengere* nzeru za nthawi* ino, koma khalani munthu watsopano posintha kwambiri maganizo anu,+ kuti muzindikire chifuniro cha Mulungu,+ chabwino, chovomerezeka ndi changwiro.

3 Chifukwa cha kukoma mtima kwakukulu kumene Mulungu anandisonyeza, ndikuuza aliyense wa inu kumeneko kuti musamadziganizire kuposa mmene muyenera kudziganizira.+ Koma aliyense aziganiza mwanzeru nʼkumadziweruza mogwirizana ndi chikhulupiriro chimene Mulungu wamupatsa.+ 4 Thupi limakhala ndi ziwalo zambiri,+ koma ziwalozo sizigwira ntchito yofanana. 5 Chimodzimodzinso ifeyo, ngakhale kuti tilipo ambiri, ndife thupi limodzi mwa Khristu ndipo ndife ziwalo zolumikizana.+ 6 Tili ndi mphatso zosiyanasiyana mogwirizana ndi kukoma mtima kwakukulu kumene tinasonyezedwa.+ Choncho kaya tili ndi mphatso ya ulosi, tiyeni tizilosera mogwirizana ndi chikhulupiriro chathu. 7 Ngati tili ndi mphatso ya utumiki, tiyeni tizichitabe utumikiwo. Amene amaphunzitsa, aziphunzitsa ndithu.+ 8 Amene amalimbikitsa, azilimbikitsa.+ Wogawa, azigawa mowolowa manja.+ Wotsogolera, azitsogolera mwakhama.+ Ndipo wosonyeza chifundo, azichita zimenezo mosangalala.+

9 Chikondi chanu chisakhale chachiphamaso.+ Muzinyansidwa ndi zoipa+ nʼkumayesetsa kuchita zabwino. 10 Pokonda abale, muzikhala ndi chikondi chenicheni. Pa nkhani yosonyezana ulemu, muziyamba ndi inuyo.+ 11 Khalani akhama osati aulesi.+ Yakani ndi mzimu.+ Tumikirani Yehova* monga akapolo.+ 12 Kondwerani chifukwa cha chiyembekezo. Muzipirira mavuto.+ Muzilimbikira kupemphera.+ 13 Gawanani ndi oyera mogwirizana ndi zimene akusowa.+ Khalani ochereza.+ 14 Pitirizani kudalitsa anthu amene akukuzunzani.+ Muzidalitsa, osati kutemberera.+ 15 Muzisangalala ndi anthu amene akusangalala ndipo muzilira ndi anthu amene akulira. 16 Muziona ena mmene inuyo mumadzionera. Musamaganize modzikuza, koma khalani ndi mtima wodzichepetsa.+ Musamadzione ngati anzeru.+

17 Musamabwezere choipa pa choipa.+ Muziganizira zimene anthu onse amaziona kuti ndi zabwino. 18 Ngati nʼkotheka, yesetsani mmene mungathere kuti muzikhala mwamtendere ndi anthu onse.+ 19 Okondedwa, musamabwezere zoipa, koma siyirani malo mkwiyo wa Mulungu.+ Chifukwa Malemba amati: “‘Kubwezera ndi kwanga, ndidzawabwezera ndine,’ watero Yehova.”*+ 20 Koma “ngati mdani wako ali ndi njala, umʼpatse chakudya. Ngati ali ndi ludzu, umʼpatse chakumwa. Chifukwa ukatero udzamuunjikira makala a moto pamutu pake.”*+ 21 Musalole kuti choipa chikugonjetseni, koma pitirizani kugonjetsa choipa pochita chabwino.+

13 Munthu aliyense azimvera olamulira akuluakulu,+ chifukwa palibe ulamuliro umene ungakhalepo kupatulapo ngati Mulungu waulola.+ Olamulira amene alipowa ali mʼmaudindo awo osiyanasiyana mololedwa ndi Mulungu.+ 2 Choncho amene akutsutsana ndi ulamuliro, akutsutsana ndi zimene Mulungu anakonza. Amene akutsutsana ndi zimene Mulungu anakonza adzalandira chiweruzo. 3 Chifukwa olamulira amaopsa ngati ukuchita zoipa, osati ngati ukuchita zabwino.+ Choncho kodi ukufuna kuti usamaope olamulira? Pitiriza kuchita zabwino,+ ndipo olamulira adzakutamanda. 4 Olamulirawo ndi mtumiki wa Mulungu kuti zinthu zikuyendere bwino. Koma ngati ukuchita zoipa, chita mantha chifukwa sagwira lupanga pachabe, popeza iwo ndi mtumiki wa Mulungu wosonyeza mkwiyo wa Mulungu kwa munthu wochita zoipa.

5 Choncho pali chifukwa chabwino choti muzigonjera, osati chabe chifukwa choopa mkwiyowu koma chifukwanso cha chikumbumtima chanu.+ 6 Nʼchifukwa chake mumakhomanso misonkho, popeza iwo ndi antchito a Mulungu otumikira anthu ndipo akukwaniritsa cholinga chimenechi nthawi zonse. 7 Muzipereka kwa onse zimene amafuna. Amene amafuna msonkho, mʼpatseni msonkho.+ Amene amafuna ndalama ya chiphaso, mʼpatseni ndalama ya chiphaso. Amene amafuna kuopedwa, muopeni.+ Amene amafuna kupatsidwa ulemu, mʼpatseni ulemu wake.+

8 Anthu inu musamakhale ndi ngongole iliyonse kwa munthu aliyense, kupatulapo kukondana,+ popeza amene amakonda munthu mnzake wakwaniritsa lamulo.+ 9 Chifukwa malamulo onena kuti, “usachite chigololo,+ usaphe munthu,+ usabe,+ usasirire mwansanje,”+ ndiponso lamulo lina lililonse limene lilipo, chidule chake chili mʼmawu awa akuti: “Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.”+ 10 Chikondi sichilimbikitsa munthu kuchitira mnzake zoipa,+ choncho chikondi chimathandiza munthu kuti akwaniritse lamulo.+

11 Chitani zimenezi, makamakanso chifukwa chakuti nyengo ino mukuidziwa, kuti tili kale mu nthawi yoti mudzuke ku tulo,+ chifukwa panopa chipulumutso chathu chili pafupi kwambiri kusiyana ndi nthawi imene tinakhala okhulupirira. 12 Usiku uli pafupi kutha ndipo masana ayandikira. Choncho tiyeni tivule ntchito za mdima+ ndipo tivale zida za kuwala.+ 13 Tiyeni tikhale ndi khalidwe loyenera+ ngati anthu amene akuchita zinthu masana. Tizipewa maphwando oipa,* kumwa mwauchidakwa,* chiwerewere, khalidwe lopanda manyazi,*+ mikangano ndiponso nsanje.+ 14 Koma valani Ambuye Yesu Khristu,+ ndipo musamakonzekere kuchita zimene thupi limalakalaka.+

14 Landirani munthu amene ali ndi chikhulupiriro chofooka,+ koma musamaweruze amene ali ndi maganizo osiyana ndi anu. 2 Wina ali ndi chikhulupiriro chakuti angadye china chilichonse, koma munthu wofooka amangodya zamasamba. 3 Amene amadya chilichonse, asamanyoze amene sadya, ndipo wosadyayo asamaweruze amene amadya chilichonse,+ popeza iye analandiridwa ndi Mulungu. 4 Ndiwe ndani kuti uweruze wantchito wa mnzako?+ Ndi udindo wa bwana wake kumuweruza kuti ndi wolakwa kapena wosalakwa+ chifukwa Yehova* akhoza kumuthandiza kuti zimuyendere bwino.

5 Wina amaona tsiku lina ngati loposa linzake,+ koma wina amaona kuti masiku onse ndi ofanana.+ Munthu aliyense azitsimikiza kuti zimene akukhulupirira nʼzolondola. 6 Amene amaona kuti tsiku lina ndi lofunika amachita zimenezo pofuna kulemekeza Yehova.* Amene amadya chakudya chilichonse, amadya kuti alemekeze Yehova,*+ chifukwa amayamika Mulungu. Amene sadya, nayenso sadya pofuna kulemekeza Yehova,* chifukwa amayamikanso Mulungu.+ 7 Kunena zoona, palibe aliyense wa ife amene amakhala ndi moyo kuti adzilemekeze yekha,+ ndipo palibe amene amafa kuti adzilemekeze yekha. 8 Tikakhala ndi moyo, timakhalira moyo Yehova,*+ ndipo tikafa, timafera Yehova.* Choncho kaya tikhale ndi moyo kapena tife, ndife a Yehova.*+ 9 Nʼchifukwa chake Khristu anafa nʼkukhalanso ndi moyo, kuti akhale Ambuye wa akufa ndiponso wa amoyo.+

10 Nanga nʼchifukwa chiyani umaweruza mʼbale wako?+ Kapenanso nʼchifukwa chiyani umanyoza mʼbale wako? Popeza tonse tidzaima patsogolo pa mpando woweruzira wa Mulungu.+ 11 Malembatu amati: “‘Pali ine Mulungu wamoyo,’+ watero Yehova,* ‘bondo lililonse lidzandigwadira, ndipo lilime lililonse lidzavomereza poyera kuti ndine Mulungu.’”+ 12 Choncho aliyense wa ife adzayankha yekha kwa Mulungu.+

13 Ndiye tisamaweruzane,+ koma mʼmalomwake tsimikizani mtima kuti simukuchita chilichonse chimene chingakhumudwitse kapena kupunthwitsa mʼbale wanu.+ 14 Ndikudziwa ndipo ndikukhulupirira mwa Ambuye Yesu kuti palibe chakudya chimene pachokha ndi chodetsedwa.+ Koma ngati munthu akuona kuti chinachake nʼchodetsedwa, kwa iyeyo ndi chodetsedwa. 15 Chifukwa ngati mʼbale wanu akukhumudwa chifukwa cha chakudya, ndiye kuti simukusonyezanso chikondi.+ Musawononge* munthu amene Khristu anamufera chifukwa cha zakudya zanu.+ 16 Choncho musalole kuti anthu azinena zoipa pa zabwino zimene mukuchita. 17 Chifukwa pa nkhani ya Ufumu wa Mulungu chofunika kwambiri si kudya ndi kumwa ayi,+ koma chilungamo, mtendere ndi chimwemwe zimene zimabwera ndi mzimu woyera. 18 Aliyense amene amatumikira Khristu mʼnjira imeneyi ndi wovomerezeka kwa Mulungu ndipo anthu amasangalala naye.

19 Choncho tiyeni tiziyesetsa kukhala mwamtendere+ ndiponso kulimbikitsana.+ 20 Siyani kuwononga ntchito ya Mulungu chifukwa cha zakudya basi.+ Zoonadi, zinthu zonse nʼzoyera, koma nʼkulakwa kudya zinthuzo ngati wina akukhumudwa nazo.+ 21 Ndi bwino kusadya nyama kapena kusamwa vinyo kapena kusachita chilichonse chimene chimakhumudwitsa mʼbale wako.+ 22 Chikhulupiriro chimene uli nacho, ukhale nacho pakati pa iweyo ndi Mulungu. Munthu amakhala wosangalala ngati sakudziimba mlandu pa zinthu zimene wasankha. 23 Koma ngati akudya kwinaku akukayikira, ameneyo watsutsidwa kale, chifukwa sakudya mogwirizana ndi chikhulupiriro. Ndithu, chilichonse chochitidwa mosemphana ndi chikhulupiriro ndi tchimo.

15 Ife amene tili olimba tiyenera kumaganizira anthu amene ali ndi chikhulupiriro chofooka,+ osati kumangodzikondweretsa tokha.+ 2 Aliyense wa ife aziyesetsa kukondweretsa mnzake ndipo azichita zinthu zomulimbikitsa.+ 3 Chifukwa ngakhale Khristu sankachita zinthu zodzikondweretsa yekha,+ koma anachita zimene Malemba amanena kuti: “Chipongwe cha anthu amene amakunyozani chandigwera.”+ 4 Zinthu zonse zimene zinalembedwa kalekale zinalembedwa kuti zitilangize.+ Malembawa amatithandiza kupirira+ ndiponso amatilimbikitsa nʼcholinga choti tikhale ndi chiyembekezo.+ 5 Choncho Mulungu amene amatipatsa mphamvu kuti tithe kupirira ndiponso amene amatitonthoza, akuthandizeni nonsenu kukhala ndi maganizo amene Khristu Yesu anali nawo, 6 kuti nonse pamodzi ndiponso mogwirizana,+ mulemekeze Mulungu, Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu.

7 Choncho muzilandirana,+ ngati mmene Khristu anatilandirira,+ kuti ulemerero upite kwa Mulungu. 8 Kunena zoona, Khristu anakhala mtumiki wa anthu odulidwa+ kuti atsimikizire kuti Mulungu ndi wokhulupirika posonyeza kuti malonjezo amene Mulunguyo anapatsa makolo awo ndi otsimikizirika.+ 9 Komanso kuti anthu a mitundu ina alemekeze Mulungu chifukwa cha chifundo chake,+ mogwirizana ndi zimene Malemba amanena kuti: “Nʼchifukwa chake ndidzakulemekezani pakati pa mitundu ya anthu ndipo ndidzaimba nyimbo zotamanda dzina lanu.”+ 10 Komanso Malemba amati: “Inu anthu a mitundu ina, kondwerani pamodzi ndi anthu ake.”+ 11 Ndiponso amati: “Tamandani Yehova,* inu mitundu yonse ya anthu ndipo anthu onse amutamande.”+ 12 Komanso Yesaya anati: “Padzakhala muzu wa Jese,+ winawake amene adzatuluke kuti alamulire mitundu.+ Chiyembekezo cha anthu a mitundu ina chidzakhala pa iyeyo.”+ 13 Mulungu amene amapereka chiyembekezo akuthandizeni kukhala osangalala kwambiri komanso kukhala ndi mtendere wonse pamene mukumukhulupirira, kuti mukhale ndi chiyembekezo champhamvu mothandizidwa ndi mzimu woyera.+

14 Abale anga, ine sindikukayikira kuti ndinu okonzeka kuchita zabwino, mukudziwa zambiri komanso mukhoza kulangizana. 15 Komabe, ndakulemberani mfundo zina mosapita mʼmbali kuti ndikukumbutseninso. Ndachita zimenezi chifukwa cha kukoma mtima kwakukulu kumene Mulungu wandisonyeza. 16 Anandisonyeza kukoma mtima kumeneku kuti ndigwire ntchito yolengeza uthenga wabwino wa Mulungu monga wantchito wa Khristu Yesu, wotumikira anthu a mitundu ina.+ Ndikugwira ntchito yopatulikayi kuti anthu a mitundu inawa akhale ngati nsembe yovomerezeka kwa Mulungu+ imene yayeretsedwa ndi mzimu woyera.

17 Choncho ndikusangalala kukhala wotsatira wa Khristu Yesu komanso kugwira ntchito ya Mulungu. 18 Sindidzalankhula chilichonse chimene ndachita pandekha, koma zokhazo zimene Khristu wachita ndi kulankhula kudzera mwa ine kuti ndithandize anthu a mitundu ina kukhala omvera. 19 Iwo akhala omvera chifukwa cha zodabwitsa zamphamvu ndiponso zizindikiro+ zimene mzimu wa Mulungu wachita. Choncho ndalalikira mokwanira uthenga wabwino wonena za Khristu kuyambira ku Yerusalemu mpaka ku Iluriko.+ 20 Pochita zimenezi ndinatsimikiza mtima kuti ndisalengeze uthenga wabwino kumene anthu ankadziwa kale za Khristu nʼcholinga choti ndisamange pamaziko a munthu wina, 21 koma ndichite mogwirizana ndi zimene Malemba amanena kuti: “Amene sanauzidwepo za iye adzamuona, ndipo amene sanamve adzazindikira.”+

22 Nʼchifukwa chakenso ndakhala ndikulephera kubwera kwa inu. 23 Koma tsopano kulibenso gawo limene sindinafikeko mʼmadera amenewa, ndipo kwa zaka zambiri* ndakhala ndikulakalaka kufika kwanuko. 24 Choncho ndili ndi chikhulupiriro kuti ndikamadzapita ku Sipaniya ndidzaonana nanu ndipo ndikadzacheza nanu kwakanthawi, mudzandiperekeza pa ulendo wangawo. 25 Koma panopa ndatsala pangʼono kupita ku Yerusalemu kukatumikira oyera.+ 26 Abale a ku Makedoniya ndi a ku Akaya apereka mosangalala mphatso kwa oyera ena a ku Yerusalemu omwe ndi osauka.+ 27 Nʼzoona kuti achita zimenezo mwa kufuna kwawo, komabe iwo anali ndi ngongole kwa oyerawo. Chifukwa ngati anthu a mitundu ina alandirako zinthu zauzimu kuchokera kwa oyerawo, ndiye kuti nawonso ayenera kutumikira oyerawo powapatsa zinthu zofunika pa moyo.+ 28 Choncho ndikakamaliza kuwapatsa zoperekazi, ndidzadzera kwanuko popita ku Sipaniya. 29 Komanso ndikudziwa kuti ndikadzafika kwanuko ndidzafika ndi madalitso ambiri ochokera kwa Khristu.

30 Choncho abale, ndikukupemphani kudzera mwa Ambuye wathu Yesu Khristu komanso chikondi cha mzimu, kuti muzilimbikira kundipempherera kwa Mulungu ndipo nanenso ndikulimbikira kupemphera.+ 31 Tilimbikire kupemphera kuti ndikapulumutsidwe+ kwa anthu osakhulupirira a ku Yudeya ndiponso kuti oyera a ku Yerusalemu akalandire bwino mphatso imene ndatenga.+ 32 Ngati Mulungu angalole, ndidzabwera kwa inu mosangalala ndipo tidzalimbikitsana. 33 Mulungu amene amapereka mtendere akhale ndi nonsenu.+ Ame.

16 Ndikufuna kukudziwitsani za mlongo wathu Febe, amene akutumikira mumpingo wa ku Kenkereya.+ 2 Mulandireni mwa Ambuye mmene mumalandirira oyerawo ndiponso kumupatsa thandizo lililonse limene angafunikire.+ Chifukwa iyenso anateteza abale ambiri, kuphatikizapo ineyo.

3 Mundiperekere moni kwa Purisika ndi Akula,+ antchito anzanga potumikira Khristu Yesu. 4 Iwo anaika miyoyo yawo pachiswe chifukwa cha ine,+ ndipo si ine ndekha amene ndikuwayamikira, komanso mipingo yonse ya anthu a mitundu ina. 5 Ndikuperekanso moni ku mpingo umene umasonkhana mʼnyumba mwawo.+ Moni kwa wokondedwa wanga Epeneto, amene ndi chipatso choyambirira cha Khristu ku Asia. 6 Moni kwa Mariya, amene wachita zinthu zambiri pokuthandizani. 7 Moni kwa Anduroniko ndi Yuniya, omwe ndi achibale anga+ komanso akaidi anzanga. Amenewa ndi amuna odziwika kwambiri kwa atumwi ndiponso akhala ogwirizana ndi Khristu kwa nthawi yaitali kuposa ineyo.

8 Mundiperekere moni kwa Ampiliato, wokondedwa wanga mwa Ambuye. 9 Moni kwa Uribano wantchito mnzathu mwa Khristu ndiponso wokondedwa wanga Sitaku. 10 Moni kwa Apele, wokhulupirika mwa Khristu. Moni kwa anthu a mʼbanja la Arisitobulo. 11 Moni kwa wachibale wanga Herodiona. Moni kwa anthu a mʼbanja la Narikiso omwe ndi otsatira a Ambuye. 12 Moni kwa Turufena ndi Turufosa, azimayi ogwira ntchito mwakhama potumikira Ambuye. Moni kwa Peresida, wokondedwa wathu. Mayi ameneyu wagwira ntchito mwakhama potumikira Ambuye. 13 Moni kwa Rufu, wosankhidwa mwa Ambuye. Moninso kwa mayi ake amenenso ndi mayi anga. 14 Moni kwa Asunkirito, Felego, Heme, Pateroba, Heremase ndiponso abale amene ali nawo limodzi. 15 Moni kwa Filologo ndi Yuliya, Nerea ndi mchemwali wake komanso Olumpa ndi oyera onse amene ali nawo limodzi. 16 Mupatsane moni mwachikondi. Mipingo yonse ya Khristu ikupereka moni.

17 Tsopano ndikukulimbikitsani abale, kuti musamale ndi amene amagawanitsa anthu ndiponso kuchita zinthu zokhumudwitsa ena. Zimenezi ndi zosemphana ndi zimene munaphunzira, choncho muziwapewa.+ 18 Chifukwa anthu oterowo si akapolo a Ambuye wathu Khristu, koma a mimba zawo. Ndipo amagwiritsa ntchito mawu okopa ndiponso achinyengo kuti apusitse anthu oona mtima. 19 Anthu onse akudziwa kuti ndinu omvera ndipo ndikusangalala nanu chifukwa cha zimenezi. Koma ndikufuna kuti mukhale anzeru pa zinthu zabwino koma osadziwa kanthu pa zinthu zoipa.+ 20 Mulungu amene amapereka mtendere aphwanya Satana+ pansi pa mapazi anu posachedwapa. Kukoma mtima kwakukulu kwa Ambuye wathu Yesu kukhale nanu.

21 Wantchito mnzanga Timoteyo akupereka moni, chimodzimodzinso Lukiyo, Yasoni ndi Sosipato omwe ndi achibale anga.+

22 Ineyo Teritio, amene ndalemba kalatayi, ndikuti moni mwa Ambuye.

23 Gayo,+ amene ndikukhala kunyumba kwawo amenenso mpingo umasonkhana kunyumba kwawo, akupereka moni. Nayenso Erasito woyangʼanira mzinda, ndi Kwarito mchimwene wake akupereka moni. 24*⁠——

25 Mulungu angakulimbitseni pogwiritsa ntchito uthenga wabwino umene ndikulengeza ndiponso uthenga wonena za Yesu Khristu umene ukulalikidwa. Uthengawu ndi wogwirizana ndi zimene zaululidwa zokhudza chinsinsi chopatulika+ chimene chakhala chobisika kwa nthawi yaitali. 26 Koma tsopano chinsinsi chimenechi chaululidwa ndipo anthu a mitundu yonse achidziwa kudzera mʼMalemba aulosi. Zimenezi nʼzogwirizana ndi lamulo la Mulungu wamuyaya. Cholinga chake nʼchakuti anthu a mitundu yonse azimumvera mwa chikhulupiriro. 27 Kwa Mulungu wanzeru yekhayo,+ kukhale ulemerero mpaka kalekale kudzera mwa Yesu Khristu. Ame.

Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”

Kapena kuti, “kusilira kwa nsanje.”

Kapena kuti, “Kukhosi kwawo.”

Onani Zakumapeto A5.

Kapena kuti, “ngati ngongole.”

Kapena kuti, “aphimbidwa.”

Onani Zakumapeto A5.

Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”

Mabaibulo ena amati, “tili ndi mtendere.”

Mabaibulo ena amati, “timasangalala.”

Mabaibulo ena amati, “timasangalala.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Pamene tinali ofooka.”

Kapena kuti, “wamasuka; wakhululukidwa.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “ziwalo.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼziwalo.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “unali wakufa.”

Kapena kuti, “Ndimapeza lamulo lakuti.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼziwalo.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼziwalo.”

Mawu a Chiheberi kapena a Chiaramu otanthauza “Ababa.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “amene akuthamanga.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “ziwiya za mkwiyo.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “ziwiya za chifundo.”

Zakumapeto A5.

Zakumapeto A5.

Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”

Onani Zakumapeto A5.

Onani Zakumapeto A5.

Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”

Onani Zakumapeto A5.

Onani Zakumapeto A5.

Kapena kuti, “Musamaumbidwe.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Onani Zakumapeto A5.

Onani Zakumapeto A5.

Kutanthauza kufewetsa ndiponso kusungunula mtima wa munthu wovuta.

Kapena kuti, “maphwando aphokoso.”

Mawu a Chigiriki amene amasuliridwa kuti “kumwa mwauchidakwa” amatanthauza kumwa mowa kwambiri ndiponso mosadziletsa nʼcholinga chofuna kuledzera.

MʼChigiriki a·sel′gei·a. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Onani Zakumapeto A5.

Onani Zakumapeto A5.

Onani Zakumapeto A5.

Onani Zakumapeto A5.

Onani Zakumapeto A5.

Onani Zakumapeto A5.

Onani Zakumapeto A5.

Onani Zakumapeto A5.

Kutanthauza kuwononga chikhulupiriro kapena chiyembekezo cha moyo wosatha wa mʼtsogolo.

Onani Zakumapeto A5.

Mabaibulo ena amati, “zingapo.”

Onani Zakumapeto A3.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena