NUMERI
1 Yehova analankhula ndi Mose mʼchipululu cha Sinai,+ mʼchihema chokumanako.+ Analankhula naye pa tsiku loyamba la mwezi wachiwiri mʼchaka chachiwiri, atatuluka mʼdziko la Iguputo.+ Iye anati: 2 “Uwerenge+ gulu lonse la Aisiraeli* mogwirizana ndi mabanja awo, potengera nyumba za makolo awo, nʼkulemba mayina awo. Uwerenge amuna onse, mmodzi ndi mmodzi. 3 Iweyo ndi Aroni muwalembe mʼkaundula mogwirizana ndi magulu awo.* Uwerenge onse kuyambira azaka 20 kupita mʼtsogolo,+ amene ali oyenera kupita kunkhondo mu Isiraeli.
4 Mutenge amuna ena kuti akuthandizeni. Mutenge mwamuna mmodzi pafuko lililonse ndipo akhale mtsogoleri wa nyumba ya makolo ake.+ 5 Mayina a amuna amene akuthandizeni ndi awa: kuchokera ku fuko la Rubeni, Elizuri+ mwana wa Sedeuri, 6 kuchokera ku fuko la Simiyoni, Selumiyeli+ mwana wa Zurisadai, 7 kuchokera ku fuko la Yuda, Naasoni+ mwana wa Aminadabu, 8 kuchokera ku fuko la Isakara, Netaneli+ mwana wa Zuwara, 9 kuchokera ku fuko la Zebuloni, Eliyabu+ mwana wa Heloni. 10 Pa ana a Yosefe: kuchokera ku fuko la Efuraimu,+ Elisama mwana wa Amihudi, kuchokera ku fuko la Manase, Gamaliyeli mwana wa Pedazuri, 11 kuchokera ku fuko la Benjamini, Abidana+ mwana wa Gidiyoni, 12 kuchokera ku fuko la Dani, Ahiyezeri+ mwana wa Amisadai, 13 kuchokera ku fuko la Aseri, Pagiyeli+ mwana wa Okirani, 14 kuchokera ku fuko la Gadi, Eliyasafu+ mwana wa Deyueli, 15 kuchokera ku fuko la Nafitali, Ahira+ mwana wa Enani. 16 Amenewa ndi amene anasankhidwa pa gulu la anthuwo. Iwo anali atsogoleri+ a mafuko a makolo awo, atsogoleri a anthu masauzande mu Isiraeli.”+
17 Choncho Mose ndi Aroni anatenga amuna amenewa, amene mayina awo anatchulidwa. 18 Iwo anasonkhanitsa anthu onse pa tsiku loyamba la mwezi wachiwiri kuti munthu aliyense amulembe mʼkaundula mogwirizana ndi mabanja awo ndiponso nyumba za makolo awo. Anawalemba mayina kuyambira azaka 20 kupita mʼtsogolo+ 19 mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose. Choncho iye anawerenga anthuwo mʼchipululu cha Sinai.+
20 Mbadwa za Rubeni, mwana woyamba wa Isiraeli,+ anazilemba mayina mmodzi ndi mmodzi. Anazilemba mogwirizana ndi mabanja awo ndiponso nyumba za makolo awo. Anawerenga amuna onse kuyambira azaka 20 kupita mʼtsogolo, amene anali oyenera kupita kunkhondo. 21 Anthu onse a fuko la Rubeni amene analembedwa mayina anakwana 46,500.
22 Mbadwa za Simiyoni,+ anazilemba mayina mmodzi ndi mmodzi. Anazilemba mogwirizana ndi mabanja awo ndiponso nyumba za makolo awo. Anawerenga amuna onse kuyambira azaka 20 kupita mʼtsogolo, amene anali oyenera kupita kunkhondo. 23 Anthu onse a fuko la Simiyoni amene analembedwa mayina analipo 59,300.
24 Mbadwa za Gadi+ anazilemba mayina mogwirizana ndi mabanja awo ndiponso nyumba za makolo awo. Anawerenga amuna onse kuyambira azaka 20 kupita mʼtsogolo, amene anali oyenera kupita kunkhondo. 25 Anthu onse a fuko la Gadi amene analembedwa mayina analipo 45,650.
26 Mbadwa za Yuda,+ anazilemba mayina mogwirizana ndi mabanja awo ndiponso nyumba za makolo awo. Anawerenga amuna onse kuyambira azaka 20 kupita mʼtsogolo, amene anali oyenera kupita kunkhondo. 27 Anthu onse a fuko la Yuda amene analembedwa mayina analipo 74,600.
28 Mbadwa za Isakara,+ anazilemba mayina mogwirizana ndi mabanja awo ndiponso nyumba za makolo awo. Anawerenga amuna onse kuyambira azaka 20 kupita mʼtsogolo, amene anali oyenera kupita kunkhondo. 29 Anthu onse a fuko la Isakara amene analembedwa mayina analipo 54,400.
30 Mbadwa za Zebuloni,+ anazilemba mayina mogwirizana ndi mabanja awo ndiponso nyumba za makolo awo. Anawerenga amuna onse kuyambira azaka 20 kupita mʼtsogolo, amene anali oyenera kupita kunkhondo. 31 Anthu onse a fuko la Zebuloni amene analembedwa mayina analipo 57,400.
32 Mbadwa za Yosefe za fuko la Efuraimu+ anazilemba mayina mogwirizana ndi mabanja awo ndiponso nyumba za makolo awo. Anawerenga amuna onse kuyambira azaka 20 kupita mʼtsogolo, amene anali oyenera kupita kunkhondo. 33 Anthu onse a fuko la Efuraimu amene analembedwa mayina analipo 40,500.
34 Mbadwa za Manase+ anazilemba mayina mogwirizana ndi mabanja awo ndiponso nyumba za makolo awo. Anawerenga amuna onse azaka 20 kupita mʼtsogolo, amene anali oyenera kupita kunkhondo. 35 Anthu onse a fuko la Manase amene analembedwa mayina analipo 32,200.
36 Mbadwa za Benjamini,+ anazilemba mayina mogwirizana ndi mabanja awo ndiponso nyumba za makolo awo. Anawerenga amuna onse kuyambira azaka 20 kupita mʼtsogolo, amene anali oyenera kupita kunkhondo. 37 Anthu onse a fuko la Benjamini amene analembedwa mayina analipo 35,400.
38 Mbadwa za Dani,+ anazilemba mayina mogwirizana ndi mabanja awo ndiponso nyumba za makolo awo. Anawerenga amuna onse kuyambira azaka 20 kupita mʼtsogolo, amene anali oyenera kupita kunkhondo. 39 Anthu onse a fuko la Dani amene analembedwa mayina analipo 62,700.
40 Mbadwa za Aseri,+ anazilemba mayina mogwirizana ndi mabanja awo ndiponso nyumba za makolo awo. Anawerenga amuna onse kuyambira azaka 20 kupita mʼtsogolo, amene anali oyenera kupita kunkhondo. 41 Anthu onse a fuko la Aseri amene analembedwa mayina analipo 41,500.
42 Mbadwa za Nafitali,+ anazilemba mayina mogwirizana ndi mabanja awo ndiponso nyumba za makolo awo. Anawerenga amuna onse azaka 20 kupita mʼtsogolo, amene anali oyenera kupita kunkhondo. 43 Anthu onse a fuko la Nafitali amene analembedwa mayina analipo 53,400.
44 Awa ndi amuna amene Mose ndi Aroni anawalemba mayina mothandizidwa ndi atsogoleri 12 a Isiraeli. Mtsogoleri aliyense ankaimira nyumba ya makolo ake. 45 Aisiraeli onse kuyambira azaka 20 kupita mʼtsogolo, amene anali oyenera kupita kunkhondo mu Isiraeli, analembedwa mayina mogwirizana ndi nyumba za makolo awo. 46 Anthu onse amene analembedwa mayina anakwana 603,550.+
47 Koma Alevi,+ mogwirizana ndi fuko la makolo awo, sanawawerenge pamodzi ndi anthu enawo.+ 48 Choncho Yehova anauza Mose kuti: 49 “Anthu a fuko la Levi okha usawalembe mayina, ndipo usaphatikize chiwerengero chawo pamodzi ndi cha Aisiraeli enawo.+ 50 Uike Alevi kuti aziyangʼanira chihema cha Umboni+ ndi ziwiya zake zonse komanso chilichonse cha mmenemo.+ Iwowo ndi amene azinyamula chihemacho ndi ziwiya zake zonse.+ Ndi amenenso azitumikira pachihemapo+ ndipo azimanga misasa yawo mozungulira chihemacho.+ 51 Nthawi zonse mukamasamutsa chihema, Aleviwo azichipasula,+ ndipo mukafika pomanga msasa, Alevi ndi amene azimanga chihemacho. Munthu aliyense amene si Mlevi akayandikira chihemacho aziphedwa.+
52 Aisiraeli azimanga matenti awo mogwirizana ndi msasa wawo, munthu aliyense mogwirizana ndi gulu lake la mafuko atatu,+ potengera magulu awo.* 53 Alevi azimanga matenti awo mozungulira chihema cha Umboni kuti mkwiyo wa Mulungu usayakire Aisiraeli.+ Aleviwo ndi amene ali ndi udindo wosamalira* chihema cha Umbonicho.”+
54 Aisiraeli anachita zonse mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose. Anachitadi zomwezo.
2 Tsopano Yehova analankhula ndi Mose ndi Aroni kuti: 2 “Aisiraeli azikhoma matenti awo, pamalo amene gulu lawo la mafuko atatu+ lapatsidwa, munthu aliyense azikhala pafupi ndi chizindikiro cha nyumba ya makolo ake. Iwo azikhoma matenti awo mozungulira chihema chokumanako komanso moyangʼana chihemacho.
3 Amene azimanga msasa wawo kumʼmawa kotulukira dzuwa ndi gulu la mafuko atatu la Yuda ndi magulu awo.* Mtsogoleri wa ana a Yuda ndi Naasoni,+ mwana wa Aminadabu. 4 Asilikali ake amene analembedwa mayina alipo 74,600.+ 5 Pafupi ndi fuko limeneli kuzikhala fuko la Isakara. Mtsogoleri wa ana a Isakara ndi Netaneli,+ mwana wa Zuwara. 6 Asilikali ake amene analembedwa mayina alipo 54,400.+ 7 Kenako pazibwera fuko la Zebuloni. Mtsogoleri wa ana a Zebuloni ndi Eliyabu,+ mwana wa Heloni. 8 Asilikali ake amene analembedwa mayina alipo 57,400.+
9 Asilikali onse a gulu la Yuda amene analembedwa mayina alipo 186,400. Amenewa azikhala oyamba kunyamuka.+
10 Amene azimanga msasa wawo kumʼmwera ndi gulu la mafuko atatu la Rubeni+ ndi magulu awo.* Mtsogoleri wa ana a Rubeni ndi Elizuri,+ mwana wa Sedeuri. 11 Asilikali ake amene analembedwa mayina alipo 46,500.+ 12 Pafupi ndi fuko limeneli pazikhala fuko la Simiyoni. Mtsogoleri wa ana a Simiyoni ndi Selumiyeli,+ mwana wa Zurisadai. 13 Asilikali ake amene analembedwa mayina alipo 59,300.+ 14 Kenako pazibwera fuko la Gadi. Mtsogoleri wa ana a Gadi ndi Eliyasafu,+ mwana wa Reueli. 15 Asilikali ake amene analembedwa mayina alipo 45,650.+
16 Asilikali onse a gulu la Rubeni amene analembedwa mayina alipo 151,450. Amenewa azikhala achiwiri kunyamuka.+
17 Posamutsa chihema chokumanako,+ gulu la Alevi lizikhala pakati pa magulu enawo.
Dongosolo limene azitsatira posamuka,+ ndi limenenso azitsatira pomanga misasa yawo, aliyense pamalo ake, mogwirizana ndi gulu lawo la mafuko atatu.
18 Amene azimanga msasa wawo kumadzulo ndi gulu la mafuko atatu la Efuraimu ndi magulu awo.* Mtsogoleri wa ana a Efuraimu ndi Elisama,+ mwana wa Amihudi. 19 Asilikali ake amene analembedwa mayina alipo 40,500.+ 20 Pafupi ndi fuko limeneli pazibwera fuko la Manase.+ Mtsogoleri wa ana a Manase ndi Gamaliyeli,+ mwana wa Pedazuri. 21 Asilikali ake amene analembedwa mayina alipo 32,200.+ 22 Kenako pazibwera fuko la Benjamini. Mtsogoleri wa ana a Benjamini ndi Abidana,+ mwana wa Gidiyoni. 23 Asilikali ake amene analembedwa mayina alipo 35,400.+
24 Asilikali onse a gulu la Efuraimu amene anawalemba mayina alipo 108,100. Amenewa azikhala achitatu kunyamuka.+
25 Amene azimanga msasa wawo kumpoto ndi gulu la mafuko atatu la Dani ndi magulu awo.* Mtsogoleri wa ana a Dani ndi Ahiyezeri,+ mwana wa Amisadai. 26 Asilikali ake amene analembedwa mayina alipo 62,700.+ 27 Pafupi ndi fuko limeneli pazibwera fuko la Aseri. Mtsogoleri wa ana a Aseri ndi Pagiyeli,+ mwana wa Okirani. 28 Asilikali ake amene analembedwa mayina alipo 41,500.+ 29 Kenako pazibwera fuko la Nafitali. Mtsogoleri wa ana a Nafitali ndi Ahira,+ mwana wa Enani. 30 Asilikali ake amene analembedwa mayina alipo 53,400.+
31 Asilikali onse a gulu la Dani amene analembedwa mayina alipo 157,600. Amenewa azikhala omalizira kunyamuka,+ mogwirizana ndi magulu a Aisiraeli a mafuko atatuatatu.”
32 Amenewa ndi Aisiraeli amene mayina awo analembedwa, mogwirizana ndi nyumba ya makolo awo. Asilikali onse amene analembedwa mayina mʼmagulu onse, analipo 603,550.+ 33 Koma Alevi sanawawerenge+ pamodzi ndi Aisiraeli enawo,+ mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose. 34 Aisiraeli anachita zonse mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose. Dongosolo limene analitsatira pomanga misasa yawo mʼmagulu a mafuko atatu,+ ndi limenenso anatsatira posamuka,+ aliyense mʼbanja lake mogwirizana ndi nyumba ya makolo ake.
3 Iyi ndi mbiri ya mbadwa za* Aroni ndi Mose pa nthawi imene Yehova analankhula ndi Mose mʼphiri la Sinai.+ 2 Mayina a ana a Aroni anali awa: woyamba Nadabu kenako Abihu,+ Eleazara+ ndi Itamara.+ 3 Ana a Aroni mayina awo anali amenewa. Iwo anali ansembe odzozedwa amene anaikidwa* kuti akhale ansembe.+ 4 Koma Nadabu ndi Abihu anafa pamaso pa Yehova atapereka moto wosaloledwa kwa Yehova+ mʼchipululu cha Sinai, ndipo iwo anafa opanda ana. Pomwe Eleazara+ ndi Itamara+ anapitiriza kutumikira monga ansembe limodzi ndi Aroni bambo awo.
5 Kenako Yehova anauza Mose kuti: 6 “Itanitsa fuko la Levi+ ndipo uwapereke kwa wansembe Aroni kuti azimutumikira.+ 7 Iwo azikwaniritsa udindo wawo pomuthandiza komanso potumikira gulu lonse pa ntchito zapachihema chokumanako. 8 Azisamalira ziwiya zonse+ zapachihema chokumanako, komanso kukwaniritsa udindo wawo wotumikira Aisiraeli pogwira ntchito zapachihema.+ 9 Upereke Alevi kwa Aroni ndi ana ake. Amenewa ndi amene aperekedwa. Aperekedwa kwa iye kuchokera kwa Aisiraeli.+ 10 Uike Aroni ndi ana ake kuti akhale ansembe, ndipo azigwira ntchito zawo zaunsembe.+ Munthu wamba* aliyense amene wayandikira malowo, aziphedwa.”+
11 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 12 “Ine ndasankha Alevi pakati pa Aisiraeli mʼmalo mwa ana onse oyamba kubadwa* a Aisiraeli+ ndipo Aleviwo adzakhala anga. 13 Mwana aliyense woyamba kubadwa ndi wanga.+ Pa tsiku limene ndinapha mwana aliyense woyamba kubadwa mʼdziko la Iguputo,+ ndinapatula mwana aliyense woyamba kubadwa pakati pa Aisiraeli kuti akhale wanga, kuyambira munthu mpaka chiweto.+ Amenewa azikhala anga. Ine ndine Yehova.”
14 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose mʼchipululu cha Sinai+ kuti: 15 “Uwerenge ana a Levi potengera nyumba ya makolo awo komanso mabanja awo. Uwerenge mwamuna aliyense kuyambira wa mwezi umodzi kupita mʼtsogolo.”+ 16 Choncho Mose anawerenga Aleviwo pomvera zimene Yehova anamulamula. 17 Mayina a ana a Levi anali awa: Gerisoni, Kohati ndi Merari.+
18 Mayina a ana a Gerisoni, potengera mabanja awo ndi awa: Libini ndi Simeyi.+
19 Ana a Kohati, potengera mabanja awo, anali Amuramu, Izara, Heburoni ndi Uziyeli.+
20 Ana a Merari, potengera mabanja awo, anali Mali+ ndi Musi.+
Mabanja a Alevi anali amenewa potengera nyumba za makolo awo.
21 Mabanja a Alibini+ ndi Asimeyi anachokera mwa Gerisoni. Amenewa ndi amene anali mabanja a Agerisoni. 22 Amuna onse amene anawerengedwa kuyambira a mwezi umodzi kupita mʼtsogolo anakwana 7,500.+ 23 Mabanja a Agerisoni ankamanga misasa yawo kumbuyo kwa chihema,+ mbali yakumadzulo. 24 Mtsogoleri wa nyumba ya Agerisoni anali Eliyasafu, mwana wa Layeli. 25 Ntchito imene ana a Gerisoni+ anapatsidwa pachihema chokumanako inali yosamalira chihema+ ndi nsalu yoyala pachihemacho, nsalu yake yophimba,+ nsalu yotchinga pakhomo,+ 26 nsalu+ za mpanda wa bwalo, nsalu yotchinga+ pakhomo la bwalo lozungulira chihema ndi guwa lansembe, zingwe za chinsalu chake, komanso ntchito zonse zokhudza zinthu zimenezi.
27 Mabanja a Aamuramu, Aizara, Aheburoni ndi Auziyeli anachokera mwa Kohati.+ Amenewa ndi amene anali mabanja a Akohati. 28 Amuna onse amene anawerengedwa, kuyambira a mwezi umodzi kupita mʼtsogolo, analipo 8,600. Amenewa ntchito yawo inali kutumikira pamalo oyera.+ 29 Mabanja a ana a Kohati ankamanga msasa wawo kumʼmwera kwa chihema.+ 30 Mtsogoleri wa nyumba ya mabanja a Akohati anali Elizafana, mwana wa Uziyeli.+ 31 Ntchito yawo inali yosamalira likasa,+ tebulo,+ choikapo nyale,+ maguwa ansembe,+ ziwiya+ zimene ankagwiritsa ntchito potumikira mʼmalo oyerawo, nsalu yotchinga+ komanso ntchito zonse zokhudza zinthu zimenezi.+
32 Mkulu wa atsogoleri onse a Alevi anali Eleazara,+ mwana wa wansembe Aroni. Iye ndi amene ankayangʼanira anthu onse amene ankatumikira pamalo oyera.
33 Mabanja a Amali ndi Amusi anachokera mwa Merari. Amenewa ndi amene anali mabanja a Amerari.+ 34 Amuna onse amene anawerengedwa, kuyambira a mwezi umodzi kupita mʼtsogolo analipo 6,200.+ 35 Mtsogoleri wa nyumba ya mabanja a Merari anali Zuriyeli, mwana wa Abihaili. Iwo ankamanga msasa wawo kumpoto kwa chihema.+ 36 Ntchito imene ana a Merari anapatsidwa inali yosamalira mafelemu+ a chihema, ndodo+ zake, zipilala+ zake, zitsulo zokhazikapo mafelemu ndi zipilala, ziwiya zake zonse+ ndi ntchito zonse zokhudza zinthu zimenezi.+ 37 Ankasamaliranso zipilala za mpanda wozungulira bwalo, zitsulo zokhazikapo zipilalazo+ komanso zikhomo ndi zingwe zake.
38 Amene ankamanga msasa wawo kumʼmawa kwa chihema, kumbali yotulukira dzuwa, anali Mose ndi Aroni, ndiponso ana a Aroni. Ntchito yawo inali kutumikira mʼmalo opatulika, mʼmalo mwa Aisiraeli. Munthu wamba aliyense* amene wayandikira malowo, ankayenera kuphedwa.+
39 Amuna onse afuko la Levi amene Mose ndi Aroni anawawerenga, pomvera lamulo la Yehova analipo 22,000. Anawerenga amuna onse kuyambira a mwezi umodzi kupita mʼtsogolo potengera mabanja awo.
40 Kenako Yehova anauza Mose kuti: “Uwerenge ana onse aamuna oyamba kubadwa a Aisiraeli, kuyambira a mwezi umodzi kupita mʼtsogolo+ ndipo ulembe mayina awo. 41 Unditengere Alevi kuti akhale anga mʼmalo mwa ana onse aamuna oyamba kubadwa a Aisiraeli.+ Unditengerenso ziweto zonse za Alevi mʼmalo mwa ziweto zonse zoyamba kubadwa za Aisiraeli.+ Ine ndine Yehova.” 42 Mose anawerenga ana onse aamuna oyamba kubadwa a Aisiraeli, mogwirizana ndi zimene Yehova anamulamula. 43 Ana onse aamuna oyamba kubadwa amene anawawerenga, kuyambira a mwezi umodzi kupita mʼtsogolo, anakwana 22,273.
44 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 45 “Utenge Alevi mʼmalo mwa ana onse aamuna oyamba kubadwa a Aisiraeli. Utengenso ziweto za Alevi mʼmalo mwa ziweto za Aisiraeli. Aleviwo akuyenera kukhala anga. Ine ndine Yehova. 46 Monga dipo*+ la ana aamuna oyamba kubadwa a Aisiraeli okwana 273 omwe apitirira chiwerengero cha Alevi,+ 47 utenge masekeli* 5 pa munthu aliyense,+ mogwirizana ndi muyezo wa sekeli yakumalo oyera.* Sekeli imodzi ndi yokwana magera* 20.+ 48 Ndalamazo uzipereke kwa Aroni ndi ana ake. Zikhale dipo* lowombolera Aisiraeli amene apitirira chiwerengero cha Alevi.” 49 Choncho Mose analandira ndalama zowombolera Aisiraeli amene chiwerengero chawo chinaposa cha Alevi. 50 Kwa ana aamuna oyamba kubadwa a Aisiraeli, analandira ndalama zokwana masekeli 1,365, mogwirizana ndi muyezo wa sekeli yakumalo oyera. 51 Ndiyeno Mose anapereka ndalama za dipozo kwa Aroni ndi ana ake pomvera mawu a Yehova, mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose.
4 Tsopano Yehova analankhula ndi Mose ndi Aroni kuti: 2 “Muwerenge ana onse a Kohati+ mwa ana a Levi, potengera mabanja awo komanso nyumba za makolo awo. 3 Muwerenge onse kuyambira azaka 30+ mpaka 50,+ amene ali mʼgulu la anthu amene anasankhidwa kuti azigwira ntchito mʼchihema chokumanako.+
4 Utumiki umene ana a Kohati azigwira mʼchihema chokumanako,+ womwe ndi utumiki wopatulika koposa, ndi uwu: 5 Mukamasamutsa msasa, Aroni ndi ana ake azilowa mʼchihema nʼkuchotsa katani+ ndipo aziphimba likasa+ la Umboni ndi kataniyo. 6 Aziliphimbanso ndi zikopa za akatumbu, nʼkuyalanso nsalu yabuluu pamwamba pake. Kenako azibwezeretsa mʼmalo ake ndodo zake zonyamulira.+
7 Iwo aziyalanso nsalu yabuluu patebulo la mkate wachionetsero,+ nʼkuikapo mbale, makapu, mbale zolowa ndi mitsuko ya nsembe yachakumwa.+ Mkate wachionetsero+ womwe ndi nsembe ya nthawi zonse uzikhalabe pomwepo. 8 Akatero, aziziphimba ndi nsalu yofiira kwambiri, ndiponso aziphimba tebulolo ndi zikopa za akatumbu. Kenako azibwezeretsa mʼmalo mwake ndodo zake zonyamulira.+ 9 Ndiyeno azitenga nsalu yabuluu nʼkuphimbira choikapo nyale,+ pamodzi ndi nyale zake,+ zopanira+ zake zozimitsira nyale, zoikamo phulusa la zingwe za nyale ndi ziwiya zake zonse zosungiramo mafuta ogwiritsa ntchito nthawi zonse. 10 Choikapo nyalecho pamodzi ndi zipangizo zake zonse, azizikulunga mʼchikopa cha akatumbu nʼkuziika pandodo yonyamulira. 11 Kenako, aziphimba guwa lansembe lagolide+ ndi nsalu yabuluu. Aziliphimbanso ndi zikopa za akatumbu, nʼkubwezeretsa mʼmalo mwake ndodo zake zonyamulira.+ 12 Akatero, azitenga ziwiya zonse+ zimene amagwiritsa ntchito pa utumiki wawo nthawi zonse mʼmalo oyera, nʼkuzikuta ndi nsalu yabuluu. Ndiyeno aziziphimba ndi zikopa za akatumbu, nʼkuziika pandodo yonyamulira.
13 Azichotsa phulusa* paguwa lansembe+ nʼkuyalapo nsalu ya ubweya wa nkhosa wapepo. 14 Aziikapo ziwiya zonse zimene amagwiritsa ntchito akamatumikira paguwa lansembe. Aziikapo zoikamo phulusa la zingwe za nyale, mafoloko aakulu, mafosholo, mbale zolowa ndi ziwiya zonse zapaguwa lansembe.+ Ndiyeno aziziphimba ndi zikopa za akatumbu, nʼkubwezeretsa mʼmalo mwake ndodo zake zonyamulira.+
15 Pamene mukusamutsa msasa, Aroni ndi ana ake azikhala atamaliza kuphimba zinthu za mʼmalo oyera+ ndi ziwiya zonse za mʼmalo oyerawo. Kenako ana a Kohati azibwera nʼkudzazinyamula+ koma iwo asamakhudze zinthu za mʼmalo oyerazo chifukwa akatero adzafa.+ Ana a Kohati ndi amene ali ndi udindo wonyamula zinthu zimenezi pachihema chokumanako.
16 Eleazara+ mwana wa wansembe Aroni ndi amene ali ndi udindo woyangʼanira mafuta a nyale,+ zofukiza zonunkhira,+ nsembe ya nthawi zonse yambewu ndi mafuta odzozera.+ Ali ndi udindo woyangʼanira chihema chonse ndi zinthu zonse za mmenemo, kuphatikizapo malo oyera ndi ziwiya zake.”
17 Yehova analankhulanso ndi Mose ndi Aroni kuti: 18 “Musalole kuti fuko la mabanja a Akohati+ liwonongeke pakati pa Alevi. 19 Koma uchite izi kuti iwo asaphedwe chifukwa choyandikira zinthu zopatulika koposa:+ Aroni ndi ana ake azilowa mʼchihemacho, ndipo munthu aliyense azimugawira ntchito ndi katundu woti anyamule. 20 Ana a Kohatiwo asadzalowe kuti akaone zinthu zopatulikazo ngakhale pangʼono pokha chifukwa akadzatero adzafa.”+
21 Ndiyeno Yehova analankhula ndi Mose kuti: 22 “Uwerenge ana onse a Gerisoni+ potengera nyumba za makolo awo komanso mabanja awo. 23 Muwerenge onse kuyambira azaka 30 mpaka 50, amene ali mʼgulu la anthu amene anasankhidwa kuti azigwira ntchito mʼchihema chokumanako. 24 Anthu amʼmabanja a Agerisoni anapatsidwa ntchito yosamalira ndi kunyamula zinthu izi:+ 25 Azinyamula nsalu za chihema kapena kuti chihema chokumanako,+ nsalu yophimba chihema, chophimba cha chikopa cha katumbu chomwe chili pamwamba pake+ ndi nsalu yotchinga pakhomo la chihema chokumanako.+ 26 Azinyamulanso nsalu za mpanda wa bwalo,+ nsalu yotchinga khomo la mpanda+ umene wazungulira chihema ndi guwa lansembe, zingwe zolimbitsira mpandawo, ziwiya zake zonse ndi zinthu zina zonse zimene amagwiritsa ntchito pa utumikiwu. Ntchito imene azigwira ndi imeneyi. 27 Aroni ndi ana ake aziyangʼanira ntchito imene ana a Gerisoni+ akuchita komanso katundu amene akunyamula. Aziwauza ntchito zimene azigwira ndi katundu amene azinyamula. 28 Utumiki umene mabanja a ana a Gerisoni azichita mʼchihema chokumanako+ ndi umenewu. Itamara+ mwana wa wansembe Aroni, ndi amene aziyangʼanira utumiki wawo.
29 Ana a Merari+ nawonso uwawerenge potengera mabanja awo komanso nyumba za makolo awo. 30 Muwerenge onse kuyambira azaka 30 mpaka 50, amene ali mʼgulu la anthu amene anasankhidwa kuti azigwira ntchito mʼchihema chokumanako. 31 Zinthu zimene azinyamula,+ mogwirizana ndi utumiki wawo pachihema chokumanako ndi izi: Mafelemu+ a chihema, ndodo+ zake, zipilala+ zake ndiponso zitsulo zokhazikapo zipilala ndi mafelemu.+ 32 Azinyamulanso zipilala+ zozungulira bwalo, zitsulo zokhazikapo zipilalazo,+ zikhomo+ ndi zingwe zolimbitsira mpandawo limodzi ndi zipangizo zonse zimene amagwiritsa ntchito pa utumiki umenewu. Munthu aliyense muzimupatsa katundu woti azinyamula. 33 Izi ndi zimene mabanja a ana a Merari+ azichita monga mbali ya utumiki wawo pachihema chokumanako. Itamara mwana wa wansembe Aroni,+ ndi amene aziyangʼanira utumiki wawo.”
34 Kenako Mose ndi Aroni pamodzi ndi atsogoleri+ a anthuwo, anawerenga ana a Kohati+ potengera mabanja awo ndi nyumba za makolo awo. 35 Anawerenga onse kuyambira azaka 30 mpaka 50, amene anali mʼgulu la anthu amene anasankhidwa kuti azigwira ntchito pachihema chokumanako.+ 36 Onse amene anawerengedwa, mogwirizana ndi mabanja awo, anakwana 2,750.+ 37 Amenewa ndi anthu amene anawerengedwa kuchokera mʼmabanja a ana a Kohati, onse amene ankatumikira pachihema chokumanako. Mose ndi Aroni anawawerenga pomvera zimene Yehova analamula kudzera mwa Mose.+
38 Ana a Gerisoni+ anawerengedwa potengera mabanja awo ndi nyumba za makolo awo, 39 anawerenga onse kuyambira azaka 30 mpaka 50, amene anali mʼgulu la anthu amene anasankhidwa kuti azitumikira pachihema chokumanako. 40 Onse amene anawerengedwa potengera mabanja awo ndi nyumba za makolo awo, anakwana 2,630.+ 41 Amenewa ndi anthu amene anawerengedwa kuchokera mʼmabanja a ana a Gerisoni, onse amene ankatumikira pachihema chokumanako. Mose ndi Aroni anawawerenga pomvera zimene Yehova analamula.+
42 Ana a Merari anawerengedwa potengera mabanja awo ndi nyumba za makolo awo, 43 anawerenga onse kuyambira azaka 30 mpaka 50, amene anali mʼgulu la anthu amene anasankhidwa kuti azigwira ntchito pachihema chokumanako.+ 44 Onse amene anawerengedwa mogwirizana ndi mabanja awo anakwana 3,200.+ 45 Amenewa ndi anthu amene anawerengedwa kuchokera mʼmabanja a ana a Merari, amene Mose ndi Aroni anawawerenga pomvera zimene Yehova analamula kudzera mwa Mose.+
46 Mose ndi Aroni, limodzi ndi atsogoleri a Isiraeli, anawerenga Alevi onse potengera mabanja awo komanso nyumba za makolo awo. 47 Anawerenga kuyambira azaka 30 mpaka 50, ndipo onse anasankhidwa kuti azitumikira komanso kunyamula katundu wa pachihema chokumanako.+ 48 Anthu onse amene anawerengedwa anakwana 8,580.+ 49 Anthuwa anawerengedwa pomvera zimene Yehova analamula kudzera mwa Mose, aliyense mogwirizana ndi utumiki wake komanso katundu amene ankanyamula. Anawerengedwa mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose.
5 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 2 “Lamula Aisiraeli kuti azitulutsa mumsasa munthu aliyense wakhate,+ aliyense wakukha kumaliseche+ komanso aliyense wodetsedwa chifukwa chokhudza munthu wakufa.+ 3 Kaya akhale mwamuna kapena mkazi, uziwatulutsa mumsasa kuti asadetse+ misasa ya anthu amene ine ndikukhala pakati pawo.”+ 4 Choncho Aisiraeli anachitadi zomwezo moti anatulutsa anthuwo kunja kwa msasa, mogwirizana ndi zimene Yehova anauza Mose.
5 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 6 “Uza Aisiraeli kuti, ‘Ngati mwamuna kapena mkazi wachita machimo alionse amene anthu amachita, nʼkuchita zinthu mosakhulupirika pamaso pa Yehova, munthu ameneyo wapalamula mlandu.+ 7 Munthuyo aziulula+ tchimo limene wachita. Azipereka malipiro onse a mlandu wake, komanso aziwonjezerapo limodzi mwa magawo 5 a malipirowo.+ Azipereka malipirowo kwa munthu amene wamulakwira. 8 Koma ngati munthu amene walakwiridwayo wamwalira ndipo alibe wachibale wapafupi amene angalandire malipiro a mlanduwo, malipirowo aziperekedwa kwa Yehova kuti akhale a wansembe. Munthu amene wachimwayo aziperekanso nkhosa yamphongo yoti wansembeyo amuphimbire machimo ake.+
9 Zopereka zonse za zinthu zopatulika,+ zimene Aisiraeli azipereka kwa wansembe, zizikhala zake.+ 10 Zinthu zopatulika za munthu aliyense zizikhala zake. Chilichonse chimene munthu angapereke kwa wansembe, chizikhala cha wansembeyo.’”
11 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 12 “Lankhula ndi Aisiraeli, ndipo uwauze kuti, ‘Muzichita izi ngati mkazi wazembera mwamuna wake nʼkuchita zosakhulupirika 13 mwakuti mwamuna wina wagona naye,+ koma mwamuna wake sanadziwe komanso palibe aliyense amene wadziwa. Muzichita zimenezi ngati mkaziyo wadzidetsa, koma palibe munthu amene angachitire umboni za nkhaniyo komanso sanagwidwe: 14 Ngati mwamuna wake akuchita nsanje ndipo akukayikira kuti mkazi wake wachita chigololo nʼkudzidetsa pamene mkaziyo wachitadi chigololo, kapena ngati akuchita nsanje nʼkumakayikira kuti mkazi wake wachita chigololo pamene mkaziyo sanachite, 15 mwamunayo azitenga mkaziyo nʼkupita naye kwa wansembe. Azipita ndi nsembe ya mkaziyo ya ufa wosalala wokwana gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa efa.* Ufawo asamauthire mafuta kapena lubani chifukwa ndi nsembe yambewu yansanje, nsembe yambewu yokumbutsa cholakwa.
16 Wansembeyo azitenga mkaziyo nʼkumuimiritsa pamaso pa Yehova.+ 17 Kenako azitenga madzi opatulika mʼchiwiya chadothi. Azitengakonso fumbi lapansi mʼchihema, nʼkulithira mʼmadziwo. 18 Ndiyeno wansembeyo aziimiritsa mkaziyo pamaso pa Yehova nʼkumumasula chovala cha kumutu kwake. Kenako, azitenga nsembe yambewu yachikumbutso, yomwe ndi nsembe yambewu yansanje,+ nʼkuiika mʼmanja mwa mkaziyo. Wansembeyo azitenga mʼdzanja lake madzi owawa obweretsa temberero.+
19 Wansembeyo azilumbiritsa mkaziyo pomuuza kuti: “Ngati mwamuna aliyense sanagone nawe ndipo ngati sunamʼzembere mwamuna wako pamene uli mʼmanja mwake+ nʼkuchita chodetsa chilichonse, madzi owawa obweretsa tembererowa asakuvulaze. 20 Koma ngati unazembera mwamuna wako pamene uli mʼmanja mwake nʼkudzidetsa, moti wagona ndi mwamuna wina—”*+ 21 Wansembeyo azilumbiritsa mkaziyo ndi lumbiro limene likuphatikizapo temberero. Iye aziuza mkaziyo kuti: “Yehova akuike kukhala chitsanzo cha temberero ndi lumbiroli pakati pa anthu a mtundu wako. Yehova achite zimenezo pofotetsa* ntchafu* yako ndi kutupitsa mimba yako. 22 Madzi a tembererowa alowe mʼmatumbo mwako kuti akatupitse mimba yako ndi kufotetsa* ntchafu* yako.” Ndipo mkaziyo aziyankha kuti: “Zikhale momwemo! Zikhale momwemo!”*
23 Kenako wansembeyo azilemba matemberero amenewa mʼbuku ndipo aziwafufuta mʼmadzi owawa aja. 24 Akatero azimwetsa mkaziyo madzi owawa a tembererowo, ndipo madziwo akalowa mʼthupi mwake, mkaziyo azimva ululu. 25 Ndiyeno wansembeyo azitenga nsembe yambewu yansanje+ imene ili mʼmanja mwa mkaziyo, nʼkuiyendetsa uku ndi uku pamaso pa Yehova. Akatero, aziibweretsa pafupi ndi guwa lansembe. 26 Wansembeyo azitapako nsembe yambewuyo kuimira nsembe yonseyo, nʼkuiwotcha paguwa lansembe.+ Pambuyo pake, azipatsa mkaziyo madziwo kuti amwe. 27 Akamumwetsa madziwo, ngati iye anadzidetsa pogona ndi mwamuna wina, madzi a tembererowo azikhala chinthu chowawa akalowa mʼthupi mwake. Zikatero mimba yake izitupa ndipo ntchafu* yake izifota.* Mkaziyo azikhala chitsanzo cha munthu wotembereredwa pakati pa anthu a mtundu wake. 28 Koma ngati mkaziyo ali woyera chifukwa sanadzidetse, chilangocho chisamamugwere, ndipo azitha kukhala woyembekezera nʼkubereka ana.
29 Limeneli ndi lamulo pa nkhani ya nsanje,+ pamene mkazi wazembera mwamuna wake, nʼkudzidetsa ali mʼmanja mwa mwamuna wakeyo, 30 kapena ngati mwamuna akuchita nsanje ndipo akuganiza kuti mkazi wake sanayende bwino. Zikatero, mwamunayo azibwera ndi mkazi wake pamaso pa Yehova, ndipo wansembe azichita zonse zofunika pa mkaziyo mogwirizana ndi lamulo limeneli. 31 Mwamunayo adzakhala wopanda mlandu, koma mkazi wake adzalandira chilango chifukwa cha kulakwa kwake.’”
6 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 2 “Lankhula ndi Aisiraeli ndipo uwauze kuti, ‘Ngati mwamuna kapena mkazi wachita lonjezo lapadera kwa Yehova lokhala Mnaziri,*+ 3 asamamwe vinyo ndi zakumwa zina zoledzeretsa. Asamamwenso viniga* wokhala ndi vinyo, kapena viniga wochokera ku zakumwa zina zoledzeretsa,+ kapenanso madzi a mphesa. Ndiponso asamadye mphesa zaziwisi kapena zouma. 4 Masiku ake onse okhala Mnaziri, asamadye chilichonse chochokera kumtengo wa mpesa, kaya zikhale mphesa zosapsa kapena khungu lake.
5 Masiku onse a lonjezo lake lokhala Mnaziri, lezala lisamadutse mʼmutu wake.+ Azikhala woyera posiya tsitsi lakumutu kwake kuti likule mpaka masiku amene anadzipereka kwa Yehova atatha. 6 Iye asamayandikire munthu wakufa masiku onse amene wadzipereka kwa Yehova. 7 Ngakhale kuti amene amwalira ndi bambo ake, mayi ake, mchimwene wake kapena mchemwali wake, iye asamadzidetse,+ chifukwa chizindikiro cha unaziri wake kwa Mulungu chili kumutu kwake.
8 Iye ndi woyera kwa Yehova masiku onse a unaziri wake. 9 Koma ngati munthu wina wafera pambali pake+ mwadzidzidzi, moti Mnaziriyo wadetsa tsitsi limene lili ngati chizindikiro choti wadzipereka kwa Mulungu, azimeta tsitsi lakumutu kwake+ pa tsiku limene wayeretsedwa. Azilimeta pa tsiku la 7. 10 Ndipo pa tsiku la 8, azibweretsa njiwa ziwiri kapena ana a nkhunda awiri kwa wansembe pakhomo la chihema chokumanako. 11 Wansembeyo azitenga mwana mmodzi wa njiwa kapena wa nkhunda nʼkumupereka monga nsembe yamachimo. Azitenganso mwana wa njiwa kapena wa nkhunda winayo nʼkumupereka monga nsembe yopsereza kuti aphimbe machimo+ amene munthuyo anachita pokhudza munthu wakufa. Akatero aziyeretsa mutu wake pa tsikulo. 12 Munthuyo aziyambiranso masiku ake odzipereka kwa Yehova ngati Mnaziri, ndipo azibweretsa nkhosa yaingʼono yamphongo yosapitirira chaka chimodzi monga nsembe yakupalamula. Koma masiku oyamba aja sadzawerengedwa chifukwa anadetsa unaziri wake.
13 Tsopano lamulo lokhudza Mnaziri ndi ili: Pa tsiku limene masiku a unaziri+ wake atha, azimubweretsa pakhomo la chihema chokumanako. 14 Kumeneko azipereka nsembe yake kwa Yehova. Azipereka nkhosa yaingʼono yamphongo yopanda chilema, yosapitirira chaka chimodzi, monga nsembe yopsereza.+ Aziperekanso mwana wa nkhosa wamkazi wopanda chilema, wosapitirira chaka chimodzi, monga nsembe yamachimo.+ Komanso azipereka nkhosa yamphongo yopanda chilema, monga nsembe yamgwirizano.+ 15 Aziperekanso dengu la mikate yozungulira yoboola pakati yopanda zofufumitsa, yophika ndi ufa wosalala ndi yopaka mafuta, timikate topyapyala topanda zofufumitsa topaka mafuta, limodzi ndi nsembe yake yambewu+ ndiponso nsembe zake zachakumwa.+ 16 Wansembeyo azibweretsa zinthuzo pamaso pa Yehova, ndipo azimuperekera nsembe yake yamachimo ndi nsembe yake yopsereza. 17 Aziperekanso kwa Yehova nkhosa yamphongo monga nsembe yamgwirizano, limodzi ndi dengu la mikate yopanda zofufumitsa ija. Kenako wansembeyo azipereka nsembe yambewu+ ndi nsembe yachakumwa, zimene zimayendera limodzi ndi nsembe yamgwirizanoyo.
18 Kenako Mnaziriyo azimeta tsitsi lakumutu kwake+ ndipo azimetera pakhomo la chihema chokumanako. Akatero, azitenga tsitsi lakumutu kwake limene linamera pa nthawi yomwe anali Mnaziri, nʼkuliponya pamoto umene uli pansi pa nsembe yamgwirizano. 19 Wansembe azitenga mwendo wakutsogolo wa nkhosa yamphongo umene wawiritsidwa.+ Azitenganso mʼdengumo mkate woboola pakati wopanda zofufumitsa ndi kamkate kopyapyala kopanda zofufumitsa. Zinthuzi aziike mʼmanja mwa Mnaziriyo atameta chizindikiro cha unaziri wake. 20 Wansembeyo aziyendetsa zinthuzo uku ndi uku monga nsembe yoperekedwa kwa Yehova.+ Zinthuzi ziziperekedwa kwa wansembeyo ngati mphatso yopatulika, limodzi ndi chidale cha nsembe yoyendetsa uku ndi uku, komanso mwendo womwe ndi gawo lopatulika.+ Pambuyo pake munthu yemwe anali Mnaziriyo angathe kumwa vinyo.
21 Lamulo lokhudza Mnaziri+ amene wachita lonjezo ndi ili: Ngati analonjeza ndipo angakwanitse kupereka nsembe kwa Yehova, kuwonjezera pa zimene amayenera kupereka monga Mnaziri, azikwaniritsa lonjezo lake, posonyeza kuti akulemekeza lamulo la unaziri wake.’”
22 Kenako Yehova anauza Mose kuti: 23 “Uza Aroni ndi ana ake kuti, ‘Mukamadalitsa+ Aisiraeli muziwauza kuti:
24 “Yehova akudalitseni+ ndipo akutetezeni.
25 Yehova asonyeze kuti akusangalala nanu+ ndipo akukomereni mtima.
26 Yehova akuyangʼaneni mokondwera ndipo akupatseni mtendere.”’+
27 Aroni ndi ana ake azigwiritsa ntchito dzina langa podalitsa Aisiraeli+ kuti ine ndiwadalitse.”+
7 Pa tsiku limene Mose anamaliza kumanga chihema,+ anachidzoza+ nʼkuchipatula, limodzi ndi zipangizo zake zonse, guwa lansembe ndi ziwiya zake zonse.+ Atamaliza kudzoza ndi kupatula zinthu zimenezi,+ 2 atsogoleri a Isiraeli,+ omwe ndi atsogoleri a nyumba za makolo awo, anapereka zopereka zawo. Atsogoleri a mafuko amenewa, omwe ankayangʼanira anthu amene anawerengedwa aja, 3 anabweretsa zopereka zawo pamaso pa Yehova. Zoperekazo zinali ngolo 6 zotseka pamwamba ndi ngʼombe zamphongo 12. Atsogoleri awiri anapereka ngolo imodzi, ndipo mtsogoleri aliyense anapereka ngʼombe yamphongo imodzi. Zoperekazo anafika nazo pachihema. 4 Yehova anauza Mose kuti: 5 “Ulandire zinthu zimenezi kwa iwo kuti zigwiritsidwe ntchito pa utumiki wapachihema chokumanako. Uzipereke kwa Alevi ndipo aliyense umupatse mogwirizana ndi zimene zikufunika pa ntchito yake.”
6 Choncho Mose analandira ngolo ndi ngʼombezo nʼkuzipereka kwa Alevi. 7 Anapereka ngolo ziwiri ndi ngʼombe 4 zamphongo kwa ana a Gerisoni, mogwirizana ndi zimene zinkafunika pa ntchito yawo.+ 8 Ana a Merari anawapatsa ngolo 4 ndi ngʼombe zamphongo 8, mogwirizana ndi zimene zinkafunika pa ntchito yawo imene ankagwira moyangʼaniridwa ndi Itamara, mwana wa wansembe Aroni.+ 9 Koma ana a Kohati sanawapatse zinthu zimenezi, chifukwa ntchito yawo inali yokhudza utumiki wapamalo oyera.+ Iwo ankanyamula zinthu zopatulika pamapewa awo.+
10 Tsopano atsogoleriwo anapereka zopereka zawo pamwambo wotsegulira+ guwa lansembe, pa tsiku limene guwalo linadzozedwa. Atsogoleriwo atabweretsa zopereka zawozo paguwa lansembe, 11 Yehova anauza Mose kuti: “Mtsogoleri mmodzi patsiku, kwa masiku otsatizana, azipereka zopereka zake kuti zigwiritsidwe ntchito potsegulira guwa lansembe.”
12 Amene anapereka zopereka zake pa tsiku loyamba anali Naasoni,+ mwana wa Aminadabu, wa fuko la Yuda. 13 Iye anapereka mbale yaikulu imodzi yasiliva yolemera masekeli* 130, ndiponso mbale yolowa imodzi yasiliva yolemera masekeli 70, mogwirizana ndi muyezo wa sekeli lakumalo oyera.*+ Mbale ziwiri zonsezo zinali zodzaza ndi ufa wosalala wothira mafuta, wa nsembe yambewu.+ 14 Anaperekanso kapu imodzi* yagolide yolemera masekeli 10, yodzaza ndi zofukiza. 15 Komanso anapereka ngʼombe yaingʼono yamphongo imodzi, nkhosa imodzi yamphongo ndi mwana wa nkhosa mmodzi wamphongo wosapitirira chaka chimodzi. Nyama zimenezi zinali za nsembe yopsereza.+ 16 Anaperekanso mbuzi yaingʼono imodzi kuti ikhale ya nsembe yamachimo.+ 17 Iye anapereka ngʼombe ziwiri, nkhosa 5 zamphongo, mbuzi 5 zamphongo, ndi ana a nkhosa 5 amphongo, aliyense wosapitirira chaka chimodzi kuti zikhale za nsembe yamgwirizano.+ Izi nʼzimene Naasoni, mwana wa Aminadabu+ anapereka.
18 Pa tsiku lachiwiri, Netaneli+ mwana wa Zuwara, mtsogoleri wa fuko la Isakara, anapereka zopereka zake. 19 Iye anapereka mbale yaikulu imodzi yasiliva yolemera masekeli 130, ndiponso mbale yolowa imodzi yasiliva yolemera masekeli 70, mogwirizana ndi muyezo wa sekeli lakumalo oyera.+ Mbale ziwiri zonsezo zinali zodzaza ndi ufa wosalala wothira mafuta, wa nsembe yambewu.+ 20 Anaperekanso kapu imodzi yagolide yolemera masekeli 10, yodzaza ndi zofukiza. 21 Komanso anapereka ngʼombe yaingʼono yamphongo imodzi, nkhosa imodzi yamphongo ndi mwana wa nkhosa mmodzi wamphongo wosapitirira chaka chimodzi. Nyama zimenezi zinali za nsembe yopsereza.+ 22 Anaperekanso mbuzi yaingʼono imodzi kuti ikhale ya nsembe yamachimo.+ 23 Iye anapereka ngʼombe ziwiri, nkhosa 5 zamphongo, mbuzi 5 zamphongo, ndi ana a nkhosa 5 amphongo, aliyense wosapitirira chaka chimodzi kuti zikhale za nsembe yamgwirizano.+ Izi nʼzimene Netaneli, mwana wa Zuwara anapereka.
24 Pa tsiku lachitatu, Eliyabu+ mwana wa Heloni, yemwe anali mtsogoleri wa ana a Zebuloni, 25 anapereka mbale yaikulu imodzi yasiliva yolemera masekeli 130, ndiponso mbale yolowa imodzi yasiliva yolemera masekeli 70, mogwirizana ndi muyezo wa sekeli lakumalo oyera.+ Mbale ziwiri zonsezo zinali zodzaza ndi ufa wosalala wothira mafuta, wa nsembe yambewu.+ 26 Anaperekanso kapu imodzi yagolide yolemera masekeli 10, yodzaza ndi zofukiza. 27 Komanso anapereka ngʼombe yaingʼono yamphongo imodzi, nkhosa imodzi yamphongo ndi mwana wa nkhosa mmodzi wamphongo wosapitirira chaka chimodzi. Nyama zimenezi zinali za nsembe yopsereza.+ 28 Anaperekanso mbuzi imodzi yaingʼono kuti ikhale ya nsembe yamachimo.+ 29 Iye anapereka ngʼombe ziwiri, nkhosa 5 zamphongo, mbuzi 5 zamphongo, ndi ana a nkhosa 5 amphongo, aliyense wosapitirira chaka chimodzi kuti zikhale za nsembe yamgwirizano.+ Izi nʼzimene Eliyabu,+ mwana wa Heloni anapereka.
30 Pa tsiku la 4, Elizuri+ mwana wa Sedeuri, yemwe anali mtsogoleri wa ana a Rubeni, 31 anapereka mbale yaikulu imodzi yasiliva yolemera masekeli 130, ndiponso mbale yolowa imodzi yasiliva yolemera masekeli 70, mogwirizana ndi muyezo wa sekeli lakumalo oyera.+ Mbale ziwiri zonsezo zinali zodzaza ndi ufa wosalala wothira mafuta, wa nsembe yambewu.+ 32 Anaperekanso kapu imodzi yagolide yolemera masekeli 10, yodzaza ndi zofukiza. 33 Komanso anapereka ngʼombe yaingʼono yamphongo imodzi, nkhosa imodzi yamphongo ndi mwana wa nkhosa mmodzi wamphongo wosapitirira chaka chimodzi. Nyama zimenezi zinali za nsembe yopsereza.+ 34 Anaperekanso mbuzi imodzi yaingʼono kuti ikhale ya nsembe yamachimo.+ 35 Iye anapereka ngʼombe ziwiri, nkhosa 5 zamphongo, mbuzi 5 zamphongo, ndi ana a nkhosa 5 amphongo, aliyense wosapitirira chaka chimodzi kuti zikhale za nsembe yamgwirizano.+ Izi nʼzimene Elizuri,+ mwana wa Sedeuri anapereka.
36 Pa tsiku la 5, Selumiyeli+ mwana wa Zurisadai, yemwe anali mtsogoleri wa ana a Simiyoni, 37 anapereka mbale yaikulu imodzi yasiliva yolemera masekeli 130, ndiponso mbale yolowa imodzi yasiliva yolemera masekeli 70, mogwirizana ndi muyezo wa sekeli lakumalo oyera.+ Mbale ziwiri zonsezo zinali zodzaza ndi ufa wosalala wothira mafuta, wa nsembe yambewu.+ 38 Anaperekanso kapu imodzi yagolide yolemera masekeli 10, yodzaza ndi zofukiza. 39 Komanso anapereka ngʼombe yaingʼono yamphongo imodzi, nkhosa imodzi yamphongo ndi mwana wa nkhosa mmodzi wamphongo wosapitirira chaka chimodzi. Nyama zimenezi zinali za nsembe yopsereza.+ 40 Anaperekanso mbuzi imodzi yaingʼono kuti ikhale ya nsembe yamachimo.+ 41 Iye anapereka ngʼombe ziwiri, nkhosa 5 zamphongo, mbuzi 5 zamphongo, ndi ana a nkhosa 5 amphongo, aliyense wosapitirira chaka chimodzi kuti zikhale za nsembe yamgwirizano.+ Izi nʼzimene Selumiyeli,+ mwana wa Zurisadai anapereka.
42 Pa tsiku la 6, Eliyasafu+ mwana wa Deyueli, yemwe anali mtsogoleri wa ana a Gadi, 43 anapereka mbale yaikulu imodzi yasiliva yolemera masekeli 130, ndiponso mbale yolowa imodzi yasiliva yolemera masekeli 70, mogwirizana ndi muyezo wa sekeli lakumalo oyera.+ Mbale ziwiri zonsezo zinali zodzaza ndi ufa wosalala wothira mafuta, wa nsembe yambewu.+ 44 Anaperekanso kapu imodzi yagolide yolemera masekeli 10, yodzaza ndi zofukiza. 45 Komanso anapereka ngʼombe yaingʼono yamphongo imodzi, nkhosa imodzi yamphongo ndi mwana wa nkhosa wamphongo wosapitirira chaka chimodzi. Nyama zimenezi zinali za nsembe yopsereza.+ 46 Anaperekanso mbuzi imodzi yaingʼono kuti ikhale ya nsembe yamachimo.+ 47 Iye anapereka ngʼombe ziwiri, nkhosa 5 zamphongo, mbuzi 5 zamphongo, ndi ana a nkhosa 5 amphongo, aliyense wosapitirira chaka chimodzi kuti zikhale za nsembe yamgwirizano.+ Izi nʼzimene Eliyasafu,+ mwana wa Deyueli anapereka.
48 Pa tsiku la 7, Elisama+ mwana wa Amihudi, yemwe anali mtsogoleri wa ana a Efuraimu, 49 anapereka mbale yaikulu imodzi yasiliva yolemera masekeli 130, ndiponso mbale yolowa imodzi yasiliva yolemera masekeli 70, mogwirizana ndi muyezo wa sekeli lakumalo oyera.+ Mbale ziwiri zonsezo zinali zodzaza ndi ufa wosalala wothira mafuta, wa nsembe yambewu.+ 50 Anaperekanso kapu imodzi yagolide yolemera masekeli 10, yodzaza ndi zofukiza. 51 Komanso anapereka ngʼombe yaingʼono yamphongo imodzi, nkhosa imodzi yamphongo ndi mwana wa nkhosa mmodzi wamphongo wosapitirira chaka chimodzi. Nyama zimenezi zinali za nsembe yopsereza.+ 52 Anaperekanso mbuzi imodzi yaingʼono kuti ikhale ya nsembe yamachimo.+ 53 Iye anapereka ngʼombe ziwiri, nkhosa 5 zamphongo, mbuzi 5 zamphongo, ndi ana a nkhosa 5 amphongo, aliyense wosapitirira chaka chimodzi kuti zikhale za nsembe yamgwirizano.+ Izi nʼzimene Elisama,+ mwana wa Amihudi anapereka.
54 Pa tsiku la 8, Gamaliyeli+ mwana wa Pedazuri, yemwe anali mtsogoleri wa ana a Manase, 55 anapereka mbale yaikulu imodzi yasiliva yolemera masekeli 130, ndiponso mbale yolowa imodzi yasiliva yolemera masekeli 70, mogwirizana ndi muyezo wa sekeli lakumalo oyera.+ Mbale ziwiri zonsezo zinali zodzaza ndi ufa wosalala wothira mafuta, wa nsembe yambewu.+ 56 Anaperekanso kapu imodzi yagolide yolemera masekeli 10, yodzaza ndi zofukiza. 57 Komanso anapereka ngʼombe yaingʼono yamphongo imodzi, nkhosa imodzi yamphongo ndi mwana wa nkhosa mmodzi wamphongo wosapitirira chaka chimodzi. Nyama zimenezi zinali za nsembe yopsereza.+ 58 Anaperekanso mbuzi imodzi yaingʼono kuti ikhale ya nsembe yamachimo.+ 59 Iye anapereka ngʼombe ziwiri, nkhosa 5 zamphongo, mbuzi 5 zamphongo, ndi ana a nkhosa 5 amphongo, aliyense wosapitirira chaka chimodzi kuti zikhale za nsembe yamgwirizano.+ Izi nʼzimene Gamaliyeli,+ mwana wa Pedazuri anapereka.
60 Pa tsiku la 9, Abidana+ mwana wa Gidiyoni, yemwe anali mtsogoleri+ wa ana a Benjamini, 61 anapereka mbale yaikulu imodzi yasiliva yolemera masekeli 130, ndiponso mbale yolowa imodzi yasiliva yolemera masekeli 70, mogwirizana ndi muyezo wa sekeli lakumalo oyera.+ Mbale ziwiri zonsezo zinali zodzaza ndi ufa wosalala wothira mafuta, wa nsembe yambewu.+ 62 Anaperekanso kapu imodzi yagolide yolemera masekeli 10, yodzaza ndi zofukiza. 63 Komanso anapereka ngʼombe yaingʼono yamphongo imodzi, nkhosa imodzi yamphongo ndi mwana wa nkhosa mmodzi wamphongo wosapitirira chaka chimodzi. Nyama zimenezi zinali za nsembe yopsereza.+ 64 Anaperekanso mbuzi imodzi yaingʼono kuti ikhale ya nsembe yamachimo.+ 65 Iye anapereka ngʼombe ziwiri, nkhosa 5 zamphongo, mbuzi 5 zamphongo, ndi ana a nkhosa 5 amphongo, aliyense wosapitirira chaka chimodzi kuti zikhale za nsembe yamgwirizano.+ Izi nʼzimene Abidana,+ mwana wa Gidiyoni anapereka.
66 Pa tsiku la 10, Ahiyezeri+ mwana wa Amisadai, yemwe anali mtsogoleri wa ana a Dani, 67 anapereka mbale yaikulu imodzi yasiliva yolemera masekeli 130, ndiponso mbale yolowa imodzi yasiliva yolemera masekeli 70, mogwirizana ndi muyezo wa sekeli lakumalo oyera.+ Mbale ziwiri zonsezo zinali zodzaza ndi ufa wosalala wothira mafuta, wa nsembe yambewu.+ 68 Anaperekanso kapu imodzi yagolide yolemera masekeli 10, yodzaza ndi zofukiza. 69 Komanso anapereka ngʼombe yaingʼono yamphongo imodzi, nkhosa imodzi yamphongo ndi mwana wa nkhosa mmodzi wamphongo wosapitirira chaka chimodzi. Nyama zimenezi zinali za nsembe yopsereza.+ 70 Anaperekanso mbuzi imodzi yaingʼono kuti ikhale ya nsembe yamachimo.+ 71 Iye anapereka ngʼombe ziwiri, nkhosa 5 zamphongo, mbuzi 5 zamphongo, ndi ana a nkhosa 5 amphongo, aliyense wosapitirira chaka chimodzi kuti zikhale za nsembe yamgwirizano.+ Izi nʼzimene Ahiyezeri,+ mwana wa Amisadai anapereka.
72 Pa tsiku la 11, Pagiyeli+ mwana wa Okirani, yemwe anali mtsogoleri wa ana a Aseri, 73 anapereka mbale yaikulu imodzi yasiliva yolemera masekeli 130, ndiponso mbale yolowa imodzi yasiliva yolemera masekeli 70, mogwirizana ndi muyezo wa sekeli lakumalo oyera.+ Mbale ziwiri zonsezo zinali zodzaza ndi ufa wosalala wothira mafuta, wa nsembe yambewu.+ 74 Anaperekanso kapu imodzi yagolide yolemera masekeli 10, yodzaza ndi zofukiza. 75 Komanso anapereka ngʼombe yaingʼono yamphongo imodzi, nkhosa imodzi yamphongo ndi mwana wa nkhosa mmodzi wamphongo wosapitirira chaka chimodzi. Nyama zimenezi zinali za nsembe yopsereza.+ 76 Anaperekanso mbuzi imodzi yaingʼono kuti ikhale ya nsembe yamachimo.+ 77 Iye anapereka ngʼombe ziwiri, nkhosa 5 zamphongo, mbuzi 5 zamphongo, ndi ana a nkhosa 5 amphongo, aliyense wosapitirira chaka chimodzi kuti zikhale za nsembe yamgwirizano.+ Izi nʼzimene Pagiyeli,+ mwana wa Okirani anapereka.
78 Pa tsiku la 12, Ahira+ mwana wa Enani, yemwe anali mtsogoleri wa ana a Nafitali, 79 anapereka mbale yaikulu imodzi yasiliva yolemera masekeli 130, ndiponso mbale yolowa imodzi yasiliva yolemera masekeli 70, mogwirizana ndi muyezo wa sekeli lakumalo oyera.+ Mbale ziwiri zonsezo zinali zodzaza ndi ufa wosalala wothira mafuta, wa nsembe yambewu.+ 80 Anaperekanso kapu imodzi yagolide yolemera masekeli 10, yodzaza ndi zofukiza. 81 Komanso anapereka ngʼombe yaingʼono yamphongo imodzi, nkhosa imodzi yamphongo ndi mwana wa nkhosa mmodzi wamphongo wosapitirira chaka chimodzi. Nyama zimenezi zinali za nsembe yopsereza.+ 82 Anaperekanso mbuzi imodzi yaingʼono kuti ikhale ya nsembe yamachimo.+ 83 Iye anapereka ngʼombe ziwiri, nkhosa 5 zamphongo, mbuzi 5 zamphongo, ndi ana a nkhosa 5 amphongo, aliyense wosapitirira chaka chimodzi kuti zikhale za nsembe yamgwirizano.+ Izi nʼzimene Ahira,+ mwana wa Enani anapereka.
84 Potsegulira guwa lansembe, pa tsiku limene guwalo linadzozedwa, atsogoleri a Isiraeli anapereka izi:+ Mbale zikuluzikulu zasiliva 12, mbale zolowa zasiliva 12 ndi makapu agolide 12.+ 85 Mbale yaikulu iliyonse yasiliva inali yolemera masekeli 130, ndipo mbale yolowa iliyonse inali yolemera masekeli 70. Siliva yense wa ziwiya zonsezi anali wolemera masekeli 2,400, mogwirizana ndi muyezo wa sekeli lakumalo oyera.+ 86 Anaperekanso makapu 12 agolide odzaza ndi zofukiza. Kapu iliyonse inali yolemera masekeli 10, mogwirizana ndi muyezo wa sekeli lakumalo oyera. Golide yense wa makapu onsewa anali wolemera masekeli 120. 87 Nyama zonse za nsembe yopsereza zinalipo ngʼombe 12 zamphongo, nkhosa 12 zamphongo ndi ana a nkhosa 12 amphongo, aliyense wosapitirira chaka chimodzi. Nyamazi anazipereka limodzi ndi nsembe zake zambewu. Atsogoleriwa anaperekanso mbuzi zingʼonozingʼono 12 za nsembe yamachimo. 88 Nyama zonse za nsembe yamgwirizano zinalipo ngʼombe 24 zamphongo, nkhosa 60 zamphongo, mbuzi 60 zamphongo ndi ana a nkhosa 60 amphongo, aliyense wosapitirira chaka chimodzi. Zimenezi ndi zimene anapereka pamwambo wotsegulira+ guwa lansembe, pambuyo poti ladzozedwa.+
89 Nthawi zonse Mose akalowa mʼchihema chokumanako kukalankhula ndi Mulungu,+ ankamva mawu akulankhula naye kuchokera pachivundikiro+ chimene chinali pamwamba pa likasa la Umboni, pakati pa akerubi+ awiri. Mulungu ankalankhula naye mwa njira imeneyi.
8 Yehova analankhula ndi Mose kuti: 2 “Lankhula ndi Aroni ndipo umuuze kuti, ‘Ukayatsa nyale, nyale zonse 7 ziziunikira malo apatsogolo pa choikapo nyalecho.’”+ 3 Choncho Aroni anachita izi: Anayatsa nyalezo kuti ziunikire malo apatsogolo pa choikapo nyalecho,+ mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose. 4 Choikapo nyalecho anachipanga chonchi: Chinali chagolide komanso chosula+ kuchokera kutsinde lake mpaka kumaluwa ake. Choikapo nyalecho anachipanga mogwirizana ndi chitsanzo chimene Yehova anaonetsa Mose mʼmasomphenya.+
5 Yehova analankhulanso ndi Mose kuti: 6 “Utenge Alevi pakati pa Aisiraeli ndipo uwayeretse.+ 7 Kuti uwayeretse uchite izi: Uwawaze madzi oyeretsera machimo ndipo iwo amete thupi lonse ndi lezala. Komanso achape zovala zawo nʼkudziyeretsa.+ 8 Kenako iwo atenge ngʼombe yaingʼono yamphongo,+ pamodzi ndi nsembe yake yambewu+ ya ufa wosalala wothira mafuta. Iweyo utenge ngʼombe inanso yaingʼono yamphongo ya nsembe yamachimo.+ 9 Ukatero, ubweretse Aleviwo kuchihema chokumanako ndipo usonkhanitse gulu lonse la Aisiraeli.+ 10 Ukamapereka Aleviwo pamaso pa Yehova, Aisiraeliwo aziika manja awo pa Aleviwo.+ 11 Ndiyeno Aroni azipereka Aleviwo kwa Yehova monga nsembe yoyendetsa uku ndi uku+ yochokera kwa Aisiraeli ndipo iwo azigwira ntchito yotumikira Yehova.+
12 Kenako Aleviwo aziika manja awo pamitu ya ngʼombe zamphongozo.+ Pambuyo pake, upereke kwa Yehova ngʼombe imodzi monga nsembe yamachimo, ndipo inayo uipereke monga nsembe yopsereza yophimbira machimo+ a Alevi. 13 Uimiritse Aleviwo pamaso pa Aroni ndi ana ake ndipo uwapereke kwa Yehova monga nsembe yoyendetsa uku ndi uku. 14 Upatule Aleviwo pakati pa Aisiraeli ndipo adzakhala anga.+ 15 Pambuyo pake, Aleviwo azitumikira pachihema chokumanako. Uzichita zimenezi powayeretsa ndi kuwapereka monga nsembe yoyendetsa uku ndi uku. 16 Amenewa ndi operekedwa. Aperekedwa kwa ine kuchokera pakati pa Aisiraeli. Ine ndikuwatenga kukhala anga mʼmalo mwa onse oyamba kubadwa* pakati pa Aisiraeli.+ 17 Mwana aliyense woyamba kubadwa pakati pa Aisiraeli ndi wanga, kaya akhale wa munthu kapena wa nyama.+ Pa tsiku limene ndinapha mwana aliyense woyamba kubadwa mʼdziko la Iguputo, ndinawapatula kuti akhale anga.+ 18 Choncho ndikutenga Alevi kuti akhale anga mʼmalo mwa ana onse oyamba kubadwa pakati pa Aisiraeli. 19 Ndidzapereka Alevi kwa Aroni ndi ana ake monga operekedwa kuchokera mwa Aisiraeli. Aleviwo adzatumikira mʼmalo mwa Aisiraeli pachihema chokumanako,+ ndipo aziphimba machimo a Aisiraeli kuti mliri usagwe pakati pawo+ chifukwa Aisiraeliwo ayandikira malo oyera.”
20 Mose ndi Aroni ndi gulu lonse la Aisiraeli, anachita zimenezi kwa Aleviwo. Aisiraeliwo anachitira Aleviwo mogwirizana ndi zonse zimene Yehova analamula Mose zokhudza Alevi. 21 Choncho Aleviwo anadziyeretsa nʼkuchapa zovala zawo.+ Pambuyo pake, Aroni anawapereka kwa Yehova monga nsembe yoyendetsa uku ndi uku.+ Kenako Aroniyo anawaphimbira machimo awo kuti awayeretse.+ 22 Ndiyeno Aleviwo analowa mʼchihema chokumanako nʼkukayamba utumiki wawo pamaso pa Aroni ndi ana ake. Anthu anachitira Aleviwo mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose zokhudza Alevi.
23 Tsopano Yehova anauza Mose kuti: 24 “Lamulo ili ndi lokhudza Alevi: Kuyambira wazaka 25 kupita mʼtsogolo azilowa mʼgulu la Alevi amene akutumikira mʼchihema chokumanako. 25 Koma akakwanitsa zaka 50, azituluka mʼgululo ndipo asamatumikirenso. 26 Iye azingothandizira abale ake amene akugwira ntchito pachihema chokumanako, koma asamatumikire kuchihemako. Izi ndi zimene uzichita ndi Alevi mogwirizana ndi ntchito zawo.”+
9 Mʼmwezi woyamba wa chaka chachiwiri, Aisiraeli atatuluka mʼdziko la Iguputo, Yehova analankhula ndi Mose mʼchipululu cha Sinai.+ Iye anati: 2 “Aisiraeli akonze nsembe ya Pasika+ pa nthawi yake imene inaikidwiratu.+ 3 Pa tsiku la 14 la mwezi uno, madzulo kuli kachisisira,* mudzakonze nsembeyo pa nthawi yake yoikidwiratu. Mudzaikonze motsatira malamulo ake onse ndiponso njira zonse za kakonzedwe kake.”+
4 Choncho Mose anauza Aisiraeli kuti akonze nsembe ya Pasika. 5 Iwo anakonza nsembe ya Pasika pa tsiku la 14 la mwezi woyamba, madzulo kuli kachisisira,* mʼchipululu cha Sinai. Aisiraeliwo anachita zonse mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose.
6 Tsopano panali amuna ena amene anadzidetsa chifukwa chokhudza mtembo wamunthu,+ moti sanathe kukonza nsembe ya Pasika pa tsikulo. Choncho amunawo anakaonekera kwa Mose ndi Aroni pa tsikulo,+ 7 nʼkunena kuti: “Ife ndife odetsedwa chifukwa takhudza munthu wakufa. Ngakhale kuti zili choncho, kodi tikuyeneradi kuletsedwa kupereka nsembe kwa Yehova pakati pa Aisiraeli pa nthawi imene inaikidwiratu?”+ 8 Ndiyeno Mose anawauza kuti: “Dikirani pomwepo, ndimve zimene Yehova angalamule zokhudza inu.”+
9 Kenako Yehova anauza Mose kuti: 10 “Uza Aisiraeli kuti, ‘Munthu aliyense pakati panu kapena pakati pa mbadwa zanu, amene wadetsedwa chifukwa chokhudza mtembo,+ kapena amene ali pa ulendo wautali, azikonzabe nsembe ya Pasika yopereka kwa Yehova. 11 Azikonza nsembeyo mʼmwezi wachiwiri+ pa tsiku la 14, madzulo kuli kachisisira.* Azidya nyama ya nsembeyo pamodzi ndi mikate yopanda zofufumitsa, ndiponso masamba owawa.+ 12 Asamasiye nyama iliyonse mpaka mʼmamawa,+ ndipo asamaphwanye fupa lake lililonse.+ Aziikonza motsatira malamulo onse a Pasika. 13 Koma ngati munthu si wodetsedwa kapena sanali pa ulendo, ndipo wanyalanyaza kukonza nsembe ya Pasika, munthuyo aziphedwa kuti asakhalenso pakati pa anthu ake,+ chifukwa sanapereke nsembeyo kwa Yehova pa nthawi imene inaikidwiratu. Munthuyo adzafa chifukwa cha tchimo lake.
14 Ngati pali mlendo amene akukhala pakati panu, iyenso azikonza nsembe ya Pasika yoti apereke kwa Yehova.+ Aziikonza motsatira malamulo onse a Pasika ndiponso kakonzedwe kake ka nthawi zonse.+ Pakhale malamulo ofanana kwa nonsenu, kaya ndi mlendo kapena mbadwa.’”+
15 Pa tsiku limene anamanga chihema,+ mtambo unaima pamwamba pa chihema cha Umbonicho. Koma kuyambira madzulo mpaka mʼmamawa, moto unkaoneka pamwamba pa chihemacho.+ 16 Zimenezi ndi zomwe zinkachitika nthawi zonse. Mtambo unkaima pamwamba pa chihemacho masana ndipo usiku pankaoneka moto.+ 17 Mtambowo ukanyamuka pamwamba pa chihemacho, Aisiraeli ankanyamuka nthawi yomweyo.+ Ndipo pamalo pamene mtambowo waima, mʼpamene Aisiraeli ankamangapo msasa.+ 18 Choncho Yehova akalamula, Aisiraeli ankanyamuka, ndipo Yehova akalamula, ankamanga msasa.+ Masiku onse amene mtambo unkakhala pamwamba pa chihemacho, iwo ankakhalabe pamsasapo. 19 Ngakhale mtambowo utakhala masiku ambiri pamwamba pa chihema, Aisiraeli ankamverabe Yehova, ndipo sankachoka pamalopo.+ 20 Nthawi zina mtambowo unkangokhala masiku owerengeka pamwamba pa chihemapo. Yehova akalamula, iwo ankakhalabe pamsasapo ndipo Yehova akalamula, iwo ankachokapo. 21 Nthawi zina mtambowo unkangokhalapo kuchokera madzulo mpaka mʼmamawa, ndipo mtambowo ukachoka mʼmamawawo, anthuwo ankanyamuka. Kaya mtambowo uchoke masana kapena usiku, iwo ankanyamuka.+ 22 Kaya mtambowo ukhale pamwamba pa chihemacho masiku awiri, mwezi, kapena masiku ambiri, Aisiraeli ankakhalabe pamsasa osachoka. Koma mtambowo ukanyamuka, iwo ankachoka. 23 Yehova akalamula, iwo ankamanga msasa, ndipo Yehova akalamula, iwo ankanyamuka. Ankamvera Yehova potsatira malangizo amene Yehova anapereka kudzera mwa Mose.
10 Kenako Yehova anauza Mose kuti: 2 “Upange malipenga awiri+ asiliva. Uchite kusula, ndipo uziwagwiritsa ntchito poitanitsa msonkhano komanso posamutsa msasa. 3 Akaliza malipenga onse awiriwo, gulu lonse lizibwera kwa iwe pakhomo la chihema chokumanako.+ 4 Koma akaliza lipenga limodzi lokha, akuluakulu amene ndi atsogoleri a masauzande a Aisiraeli, azibwera kwa iwe.+
5 Mukaliza lipenga lolira mosinthasintha, anthu amene ali mʼmisasa yakumʼmawa+ azinyamuka. 6 Mukaliza kachiwiri lipenga lolira mosinthasintha, anthu amene ali mʼmisasa yakumʼmwera+ azinyamuka. Gulu lililonse likamanyamuka, aziliza lipenga lolira mosinthasintha.
7 Poitanitsa msonkhano wa anthu onse muziliza lipenga,+ koma osati lolira mosinthasintha. 8 Ana a Aroni, omwe ndi ansembe, ndi amene aziliza malipengawo.+ Ndi lamulo kwa inu kuti muzigwiritsa ntchito malipengawa mʼmibadwo yanu yonse mpaka kalekale.
9 Ngati mukufunika kumenya nkhondo mʼdziko lanu polimbana ndi mdani amene akukuzunzani, muziliza malipengawo+ posonyeza kuti mukuitanira asilikali kunkhondo. Mukatero, Yehova Mulungu wanu adzakukumbukirani ndipo adzakupulumutsani kwa adani anuwo.
10 Komanso pa nthawi ya zisangalalo+ zanu, monga pa zikondwerero+ zanu ndi kumayambiriro kwa miyezi, muziliza malipenga popereka nsembe zanu zopsereza+ ndi zamgwirizano.+ Kulira kwa malipengawo kudzachititsa kuti Mulungu akukumbukireni. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.”+
11 Tsopano mʼchaka chachiwiri, mwezi wachiwiri, pa tsiku la 20 la mweziwo,+ mtambo uja unanyamuka pamwamba pa chihema+ cha Umboni. 12 Choncho Aisiraeli ananyamuka mʼchipululu cha Sinai potsatira dongosolo lawo lonyamukira,+ ndipo mtambowo unakaima mʼchipululu cha Parana.+ 13 Kameneka kanali koyamba kuti iwo asamuke motsatira malangizo amene Yehova anapereka kudzera mwa Mose.+
14 Choncho, gulu la mafuko atatu la ana a Yuda ndi limene linali loyamba kunyamuka potengera magulu awo.* Mtsogoleri wa gululi anali Naasoni,+ mwana wa Aminadabu. 15 Mtsogoleri wa gulu la fuko la ana a Isakara anali Netaneli,+ mwana wa Zuwara. 16 Mtsogoleri wa gulu la fuko la ana a Zebuloni anali Eliyabu,+ mwana wa Heloni.
17 Chihema chitapasulidwa,+ ana a Gerisoni+ ndi ana a Merari,+ amene ankanyamula chihemacho, ananyamuka.
18 Kenako, gulu la mafuko atatu la ana a Rubeni linanyamuka potengera magulu awo.* Mtsogoleri wa gululi anali Elizuri,+ mwana wa Sedeuri. 19 Mtsogoleri wa gulu la fuko la ana a Simiyoni anali Selumiyeli,+ mwana wa Zurisadai. 20 Mtsogoleri wa gulu la fuko la ana a Gadi anali Eliyasafu,+ mwana wa Deyueli.
21 Kenako Akohati, amene ankanyamula zinthu za mʼmalo opatulika+ ananyamuka, kuti akamakafika akapeze chihema chitamangidwa kale.
22 Ndiyeno gulu la mafuko atatu la ana a Efuraimu linanyamuka potengera magulu awo.* Mtsogoleri wa gululi anali Elisama,+ mwana wa Amihudi. 23 Mtsogoleri wa gulu la fuko la ana a Manase anali Gamaliyeli,+ mwana wa Pedazuri. 24 Mtsogoleri wa gulu la fuko la ana a Benjamini anali Abidana,+ mwana wa Gidiyoni.
25 Pomaliza, gulu la mafuko atatu la ana a Dani linanyamuka potengera magulu awo.* Iwo ndi amene ankalondera kumbuyo kwa magulu onse a mafukowo. Mtsogoleri wa gululi anali Ahiyezeri,+ mwana wa Amisadai. 26 Mtsogoleri wa gulu la fuko la ana a Aseri anali Pagiyeli,+ mwana wa Okirani. 27 Mtsogoleri wa gulu la fuko la ana a Nafitali anali Ahira,+ mwana wa Enani. 28 Dongosolo limene Aisiraeli ndi magulu awo* ankatsatira posamuka ndi limeneli.+
29 Ndiyeno Mose anauza Hobabu mwana wa mpongozi wake Reueli*+ wa ku Midiyani, kuti: “Tikusamukira kumalo amene Yehova anati, ‘Ndidzawapereka kwa inu.’+ Tiyeni tipite limodzi,+ ndipo tidzakuchitirani zabwino, chifukwa Yehova analonjeza Aisiraeli zinthu zabwino.”+ 30 Koma iye anamuyankha kuti: “Ayi, sindipita nanu kumeneko. Ndibwerera kudziko lakwathu, kwa abale anga.” 31 Komabe Mose anamupempha kuti: “Chonde musatisiye, chifukwa inu mukudziwa bwino kumene tingamange msasa mʼchipululu muno, ndipo mungamatilondolere.* 32 Ngati mungapite nafe limodzi,+ madalitso amene Yehova adzatipatse inunso mudzalandira nawo.”
33 Choncho iwo ananyamuka kuphiri la Yehova,+ nʼkuyenda ulendo wa masiku atatu. Likasa+ la pangano la Yehova linali patsogolo pawo ulendo wa masiku atatu wonsewo, mpaka atapeza malo oti amangepo msasa.+ 34 Akanyamuka pamsasa masana, mtambo wa Yehova+ unkakhala pamwamba pawo.
35 Nthawi zonse Likasa likamanyamuka, Mose ankanena kuti: “Nyamukani, inu Yehova,+ adani anu abalalike. Ndipo amene amadana nanu athawe pamaso panu.” 36 Nthawi zonse likasalo likaima, iye ankanena kuti: “Bwererani inu Yehova, kwa Aisiraeli masauzande osawerengeka.”*+
11 Tsopano anthuwo anayamba kudandaula kwambiri pamaso pa Yehova. Yehova atamva kudandaulako mkwiyo wake unayaka, ndipo moto wochokera kwa Yehova unawayakira nʼkupsereza ena mwa anthuwo kumalire a msasa. 2 Koma anthuwo atayamba kulirira Mose, iye anapembedzera Yehova+ ndipo motowo unazima. 3 Choncho malowo anawatchula kuti Tabera,* chifukwa moto wochokera kwa Yehova unawayakira pamalo amenewo.+
4 Kenako gulu la anthu a mitundu yosiyanasiyana+ lomwe linali pakati pawo linasonyeza mtima wadyera,+ ndipo Aisiraeli nawonso anayamba kulira nʼkumanena kuti: “Ndani atipatse nyama yoti tidye?+ 5 Tikukumbukira nsomba zaulere zimene tinkadya ku Iguputo, nkhaka, mavwende, adyo komanso anyezi wamitundumitundu!+ 6 Koma pano tilibe ndi mphamvu zomwe. Sitikuonanso chilichonse kupatulapo manawa.”+
7 Manawo+ anali ngati mapira,*+ ndipo ankaoneka ngati utomoni woonekera mkati ngati galasi. 8 Anthuwo ankamwazikana kukatola manawo. Akatero, ankawapera pamphero kapena kuwasinja mumtondo. Kenako ankawawiritsa mumphika, kapena kuwapanga makeke ozungulira+ ndipo ankakoma ngati keke yotsekemera yothira mafuta. 9 Mame akagwa pamsasa usiku, mananso ankagwa.+
10 Mose anamva anthu akulira mʼbanja lililonse, munthu aliyense pakhomo la tenti yake. Ndipo Yehova anakwiya kwambiri+ komanso Mose anakhumudwa kwambiri. 11 Ndiyeno Mose anauza Yehova kuti: “Nʼchifukwa chiyani mwandivutitsa chonchi ine mtumiki wanu? Nʼchifukwa chiyani mwandiumira mtima chonchi, nʼkundisenzetsa chimtolo cha anthu onsewa?+ 12 Kodi ndine ndinatenga pakati pa anthu onsewa? Ndine kodi ndinawabereka, kuti mundiuze kuti, ‘Uwanyamule pachifuwa chako mmene wantchito yolera mwana amanyamulira mwana woyamwa,’ pa ulendo wopita nawo kudziko limene munalumbira kuti mudzalipereka kwa makolo awo?+ 13 Kodi nyama yoti ndipatse anthu onsewa ndiitenga kuti? Chifukwa iwo akupitirizabe kundilirira kuti, ‘Tipatse nyama yoti tidye!’ 14 Sindingathe kuwasamalira ndekha anthu onsewa. Ntchito imeneyi yandikulira.+ 15 Ngati izi ndi zimene muzindichitira kuli bwino mungondipha pompano.+ Koma ngati mwandikomera mtima, musandionetsenso tsoka lina.”
16 Yehova anayankha Mose kuti: “Undisonkhanitsire akulu 70 pakati pa akulu a Isiraeli, amene umawaona* kuti ndi akulu komanso oyangʼanira pakati pa anthuwo.+ Upite nawo kuchihema chokumanako, ndipo akaime kumeneko limodzi ndi iwe. 17 Ine ndibwera kumeneko+ kudzalankhula nawe+ ndipo ndidzatenga gawo lina la mzimu+ umene uli pa iwe nʼkuuika pa anthuwo. Pamenepo iwo adzatha kukuthandiza kusenza udindo woyangʼanira anthuwo, kuti usausenze wekha.+ 18 Anthuwo uwauze kuti, ‘Mudziyeretse pokonzekera mawa,+ chifukwa mudya nyama. Paja mwakhala mukulirira Yehova+ kuti: “Ndani atipatse nyama yoti tidye? Ku Iguputo zinthu zinkatiyendera bwino.”+ Yehova akupatsanidi nyamayo ndipo mudya.+ 19 Nyamayo simuidya tsiku limodzi, kapena masiku awiri, kapena masiku 5, kapena masiku 10, kapenanso masiku 20 ayi, 20 koma mudzaidya kwa mwezi wonse wathunthu, mpaka idzatulukira mʼmphuno mwanu, ndipo mudzachita kunyansidwa nayo.+ Zidzatero chifukwa mwakana Yehova amene ali pakati panu, ndipo mumamulirira kuti: “Tinachokeranji ku Iguputo?”’”+
21 Ndiyeno Mose anati: “Amuna amene ndikuyenda nawo alipo 600,000,+ koma inu mwanena kuti, ‘Ndiwapatsa nyama yokwanira kudya mwezi wonse wathunthu.’ 22 Kodi titapha ziweto zonse zingawakwanire? Kapena titapha nsomba zonse zamʼnyanja, kodi zingawakwanire?”
23 Ndiyeno Yehova anayankha Mose kuti: “Kodi dzanja la Yehova ndi lalifupi?+ Tsopano uona ngati zimene ndanenazi zichitike kapena ayi.”
24 Choncho Mose anapita kukauza anthuwo mawu a Yehova. Iye anasonkhanitsa amuna 70 kuchokera pakati pa akulu a anthuwo, nʼkuwauza kuti aimirire mozungulira chihema chokumanako.+ 25 Kenako Yehova anatsika mumtambo+ nʼkulankhula naye.+ Anatengako gawo lina la mzimu+ umene unali pa Mose nʼkuuika pa aliyense wa akulu 70 amenewo. Ndipo mzimuwo utangokhala pa iwo, anayamba kuchita zinthu ngati aneneri,*+ koma anangochita zimenezi kamodzi kokhaka.
26 Ndiyeno panali amuna awiri amene anatsalira mumsasa. Mayina awo anali Eledadi ndi Medadi. Amenewanso analandira mzimuwo chifukwa anali mʼgulu la anthu amene analembedwa mayina, koma sanapite nawo kuchihema. Choncho iwonso anayamba kuchita zinthu ngati aneneri mumsasamo. 27 Ndiye mnyamata wina anathamanga kukanena kwa Mose kuti: “Eledadi ndi Medadi akuchita zinthu ngati aneneri mumsasa.” 28 Kenako Yoswa+ mwana wa Nuni, yemwe anali mtumiki wa Mose kuyambira ali mnyamata, anayankhira kuti: “Mbuyanga Mose, kawaletseni amenewo!”+ 29 Koma Mose anayankha kuti: “Kodi ukuchita nsanje chifukwa chondidera nkhawa? Ayi usatero. Ndikanakonda anthu onse a Yehova akanakhala aneneri komanso Yehova akanaika mzimu wake pa iwo!” 30 Pambuyo pake, Mose limodzi ndi akulu a Isiraeliwo anabwerera kumsasa.
31 Kenako Yehova anabweretsa mphepo yamphamvu kuchokera kunyanja. Mphepoyo inabweretsa zinziri, ndipo inazimwaza kuzungulira msasawo+ mpaka pamtunda woyenda tsiku limodzi kulowera mbali zonse za msasawo. Inazimwaza kuzungulira msasawo, moti zinaunjikana mulu wokwana pafupifupi masentimita 90* kuchokera pansi. 32 Ndiyeno anthuwo anayamba kugwira zinzirizo. Anazigwira masana onse, usiku wonse, mpakanso tsiku lotsatira osapuma. Palibe amene anagwira zosakwana mahomeri* 10 ndipo ankaziyanika paliponse, moti zinangoti mbwee, pamsasa wonsewo. 33 Koma nyamayo idakali mʼkamwa mwawo, asanaitafune nʼkomwe, mkwiyo wa Yehova unayakira anthuwo. Ndipo Yehova anayamba kuwalanga moti anthu ambiri anaphedwa.+
34 Malo amenewo anawatchula kuti Kibiroti-hatava,*+ chifukwa anakwirirapo anthu amene anasonyeza mtima wadyera.+ 35 Anthuwo atachoka pa Kibiroti-hatava, anasamukira ku Hazeroti,+ ndipo anakhala kumeneko.
12 Tsopano Miriamu ndi Aroni anayamba kumunena Mose chifukwa cha mkazi wa Chikusi+ amene anamukwatira. 2 Iwo ankanena kuti: “Kodi Yehova walankhula kudzera mwa Mose yekha? Kodi sanalankhulenso kudzera mwa ife?”+ Koma Yehova ankamvetsera.+ 3 Mose anali munthu wofatsa kwambiri kuposa anthu onse*+ amene anali padziko lapansi.
4 Kenako mwadzidzidzi Yehova anauza Mose, Aroni ndi Miriamu kuti: “Nonse atatu nyamukani, mupite kuchihema chokumanako.” Choncho onse atatu ananyamuka nʼkupita. 5 Ndiyeno Yehova anatsika mʼchipilala chamtambo+ nʼkuima pakhomo la chihema chokumanako. Kenako anaitana Aroni ndi Miriamu ndipo onse anapita. 6 Iye anawauza kuti: “Mvetserani mawu anga. Pakanakhala mneneri wa Yehova pakati panu, ndikanamudziwitsa za ine mʼmasomphenya,+ ndipo ndikanalankhula naye mʼmaloto.+ 7 Koma sindinachite zimenezo ndi mtumiki wanga Mose. Ndaika anthu anga onse Aisiraeli mʼmanja mwake.*+ 8 Ndimalankhula naye pamasomʼpamaso,*+ kumuuza zinthu momveka bwino osati mophiphiritsa, ndipo amaona maonekedwe a Yehova. Ndiye nʼchifukwa chiyani inu simunaope kumunena Mose mtumiki wanga?”
9 Choncho Yehova anawakwiyira kwambiri nʼkuchokapo. 10 Mtambo uja unachoka pamwamba pa chihemacho. Pomwepo, Miriamu anagwidwa ndi khate loyera kwambiri.+ Kenako Aroni atatembenuka nʼkumuyangʼana Miriamu, anaona kuti wachita khate.+ 11 Nthawi yomweyo Aroni anachonderera Mose kuti: “Pepani mbuyanga, chonde, musatilange chifukwa cha tchimo limene tachitali. Zimene tachitazi ndi zinthu zopusa. 12 Chonde, musamusiye Miriamu kuti akhale ngati mwana wobadwa wakufa, amene mnofu wake ndi wowola mbali ina.” 13 Ndiyeno Mose anayamba kufuulira Yehova kuti: “Chonde Mulungu wanga, muchiritseni chonde!”+
14 Yehova anauza Mose kuti: “Kodi bambo ake akanamulavulira malovu kumaso, sakanakhala wonyozeka kwa masiku 7? Ndiye mʼtulutseni akakhale kunja kwa msasa+ kwa masiku 7, pambuyo pake mumulowetsenso mumsasamo.” 15 Choncho Miriamu anatulutsidwa kukakhala kunja kwa msasa kwa masiku 7,+ ndipo anthuwo sanasamuke mpaka Miriamu atamubweretsanso mumsasa. 16 Kenako anthuwo anachoka ku Hazeroti,+ nʼkukamanga msasa mʼchipululu cha Parana.+
13 Tsopano Yehova analankhula ndi Mose kuti: 2 “Utume amuna kuti akazonde* dziko la Kanani limene ndikulipereka kwa Aisiraeli. Pa fuko lililonse utume mwamuna mmodzi, ndipo akhale mtsogoleri+ wa fuko lawo.”+
3 Choncho Mose anatumiza amunawo kuchokera kuchipululu cha Parana,+ mogwirizana ndi zimene Yehova analamula. Amuna onsewo anali atsogoleri a Aisiraeli. 4 Mayina awo ndi awa: Wa fuko la Rubeni anali Samuwa, mwana wa Zakuri. 5 Wa fuko la Simiyoni anali Safati, mwana wa Hori. 6 Wa fuko la Yuda anali Kalebe,+ mwana wa Yefune. 7 Wa fuko la Isakara anali Igali, mwana wa Yosefe. 8 Wa fuko la Efuraimu anali Hoshiya,+ mwana wa Nuni. 9 Wa fuko la Benjamini anali Paliti, mwana wa Rafu. 10 Wa fuko la Zebuloni anali Gadiyeli, mwana wa Sodi. 11 Wa fuko la Yosefe,+ kuimira fuko la Manase,+ anali Gadidi mwana wa Susi. 12 Wa fuko la Dani anali Amiyeli, mwana wa Gemali. 13 Wa fuko la Aseri anali Seturi, mwana wa Mikayeli. 14 Wa fuko la Nafitali anali Nabi, mwana wa Vopisi. 15 Wa fuko la Gadi anali Geyuweli, mwana wa Maki. 16 Mayina a amuna amene Mose anawatuma kuti akazonde dzikolo ndi amenewa. Mose anapatsa Hoshiya mwana wa Nuni dzina lakuti Yoswa.*+
17 Powatumiza kuti akazonde dziko la Kanani, Mose anawauza kuti: “Mupite kumeneko kudzera ku Negebu, ndipo kenako mukafike kudera lamapiri.+ 18 Mukaone kuti dzikolo ndi lotani.+ Mukaonenso ngati anthu amʼdzikomo ndi amphamvu kapena opanda mphamvu, ngati ali ochepa kapena ambiri. 19 Mukaone ngati dzikolo lili labwino kapena loipa, ndiponso ngati mizinda imene akukhala ilibe mipanda kapena ngati ili ndi mipanda yolimba kwambiri. 20 Komanso mukaone ngati dzikolo lili lachonde kapena lopanda chonde,+ ngati lili ndi mitengo kapena ayi. Mukalimbe mtima+ nʼkutengako zipatso zamʼdzikomo.” Imeneyi inali nthawi imene mphesa zoyamba zinkapsa.+
21 Choncho amunawo anapita kukazonda dzikolo, kuyambira kuchipululu cha Zini+ mpaka ku Rehobu,+ kufupi ndi Lebo-hamati.*+ 22 Atapita ku Negebu,+ anakafika ku Heburoni kumene kunkakhala Ahimani, Sesai ndi Talimai,+ omwe ndi Aanaki.*+ Mzinda wa Heburoni unamangidwa zaka 7 mzinda wa Zowani wa ku Iguputo usanamangidwe. 23 Atafika kuchigwa cha Esikolo,*+ anadula nthambi yokhala ndi phava limodzi lalikulu la mphesa, ndipo anthu awiri analinyamula paphewa ndi ndodo yonyamulira. Anatengakonso makangaza* ndi nkhuyu.+ 24 Malowo anawapatsa dzina lakuti chigwa cha Esikolo,*+ chifukwa chakuti Aisiraeliwo anadulapo phava la mphesa.
25 Patatha masiku 40,+ anabwerako kokazonda dziko kuja. 26 Iwo anabwerera kwa Mose ndi Aroni ndiponso gulu lonse la Aisiraeli mʼchipululu cha Parana, ku Kadesi.+ Anafotokozera gulu lonselo za ulendo wawo nʼkuwaonetsa zipatso za kudzikolo. 27 Iwo anauza Mose kuti: “Tinakalowa mʼdziko limene munatituma lija ndipo ndi dziko loyendadi mkaka ndi uchi,+ moti zipatso zake ndi izi.+ 28 Ngakhale zili choncho, anthu okhala kumeneko ndi anthu amphamvu zawo, ndipo ali ndi mizinda ikuluikulu yotchingidwa ndi mipanda yolimba kwambiri. Si zokhazo, taonanso Aanaki kumeneko.+ 29 Aamaleki+ akukhala ku Negebu.+ Ahiti, Ayebusi+ ndi Aamori+ akukhala kudera lamapiri. Akanani+ akukhala mʼmphepete mwa nyanja+ ndi mʼmphepete mwa mtsinje wa Yorodano.”
30 Kenako Kalebe anayesa kukhazika anthuwo mtima pansi pamaso pa Mose ponena kuti: “Tiyeni tipite pompano, tikatenga dzikolo kukhala lathu, chifukwa tingathe kuwagonjetsa anthuwo.”+ 31 Koma amuna amene anapita naye limodzi ananena kuti: “Sitingathe kukalimbana nawo anthuwo, chifukwa ndi amphamvu kuposa ifeyo.”+ 32 Ndipo iwo anapitiriza kuuza Aisiraeliwo lipoti loipa+ lokhudza dziko limene anakalizondalo kuti: “Dziko limene tinakalizondalo limameza anthu ake, ndipo anthu onse amene tinawaona kumeneko ndi ziphona zamatupi akuluakulu.+ 33 Tinaonakonso Anefili,* ana a Anaki+ omwe ndi mbadwa za Anefili, moti tikadziyerekezera ndi iwowo, ifeyo timangooneka ngati tiziwala. Iwonso ndi mmene amationera.”
14 Kenako gulu lonselo linayamba kudandaula mofuula, ndipo anthuwo anapitiriza kulira usiku wonse.+ 2 Aisiraeli onse anayamba kungʼungʼudzira Mose ndi Aroni,+ ndipo gulu lonselo linati: “Zikanakhala bwino tikanangofera ku Iguputo, kapena tikanangofera mʼchipululu muno. 3 Nʼchifukwa chiyani Yehova watibweretsa kudziko lino kuti tidzaphedwe ndi lupanga?+ Akazi athu ndi ana athu adzatengedwa ndi adani.+ Kodi si bwino kuti tingobwerera ku Iguputo?”+ 4 Iwo anafika ngakhale pouzana kuti: “Tiyeni tisankhe mtsogoleri, tibwerere ku Iguputo!”+
5 Mose ndi Aroni atamva zimenezi, anagwada nʼkuwerama mpaka nkhope zawo pansi pamaso pa gulu lonse la Aisiraeli. 6 Ndipo Yoswa+ mwana wa Nuni ndi Kalebe+ mwana wa Yefune, amene anakazonda nawo dzikolo, anangʼamba zovala zawo. 7 Iwo anauza gulu lonse la Aisiraeli kuti: “Dziko limene tinakalowamo nʼkulizonda ndi dziko labwino kwambiri.+ 8 Ngati Yehova akusangalala nafe, adzatilowetsadi mʼdzikolo nʼkulipereka kwa ife, dziko loyenda mkaka ndi uchi.+ 9 Koma chofunika nʼchakuti musapandukire Yehova, ndipo anthu amʼdzikolo musawaope,+ chifukwa ali ngati chakudya kwa ife. Alibenso chitetezo, koma ifeyo Yehova ali nafe.+ Musawaope.”
10 Koma gulu lonselo linayamba kunena zoti liwaponye miyala.+ Kenako, ulemerero wa Yehova unaonekera kwa Aisiraeli onse+ pamwamba pa chihema chokumanako.
11 Ndiyeno Yehova analankhula ndi Mose kuti: “Kodi anthu awa apitiriza kundinyoza mpaka liti?+ Kodi adzayamba liti kundikhulupirira pambuyo pa zizindikiro zonse zimene ndachita pakati pawo?+ 12 Ndiwagwetsera mliri ndi kuwawononga, ndipo iwe ndidzakusandutsa mtundu waukulu ndi wamphamvu kuposa iwowa.”+
13 Koma Mose anayankha Yehova kuti: “Mukatero, Aiguputo amene anthuwa munawalanditsa mʼmanja mwawo pogwiritsa ntchito mphamvu zanu, adzamva zimenezi.+ 14 Iwo akamva adzauza anthu amʼdziko lino, amenenso amva kuti inu Yehova muli pakati pa anthu anu,+ komanso kuti mumaonekera kwa iwo pamasomʼpamaso.+ Inu ndinu Yehova, ndipo mtambo wanu uli pamwamba pawo. Masana mumawatsogolera pogwiritsa ntchito chipilala cha mtambo, pamene usiku mumawatsogolera pogwiritsa ntchito chipilala cha moto.+ 15 Mukapha anthu onsewa kamodzinʼkamodzi,* mitundu imene yamva za inu idzanena kuti: 16 ‘Yehova analephera kufikitsa anthuwo kudziko limene anawalumbirira, choncho anangowaphera mʼchipululu.’+ 17 Chonde Yehova, tsopano sonyezani kuti mphamvu zanu ndi zazikulu mogwirizana ndi mmene munalonjezera kuti: 18 ‘Yehova ndi wosakwiya msanga, ndiponso wachikondi chokhulupirika chochuluka.*+ Amakhululukira zolakwa ndi machimo, koma sadzalekerera wolakwa osamupatsa chilango. Amalanga ana, zidzukulu ndi ana a zidzukuluzo chifukwa cha zolakwa za abambo awo.’+ 19 Chonde, khululukani zolakwa za anthuwa mogwirizana ndi chikondi chanu chokhulupirika chomwe ndi chachikulu, ngati mmene mwakhala mukuwakhululukira kuchokera ku Iguputo mpaka pano.”+
20 Ndiyeno Yehova anati: “Chabwino, ndawakhululukira mogwirizana ndi zimene wanena.+ 21 Komanso, pali ine Mulungu wamoyo, dziko lonse lapansi lidzadzaza ndi ulemerero wa Yehova.+ 22 Komabe anthu onse amene aona ulemerero wanga ndi zizindikiro zanga+ zimene ndinachita ku Iguputo, komanso zimene ndachita mʼchipululu, koma apitiriza kundiyesa+ maulendo 10 onsewa, ndipo sanamvere mawu anga,+ 23 sadzaliona mʼpangʼono pomwe dziko limene ndinalumbirira makolo awo. Ndithudi, onse amene sakundipatsa ulemu, sadzaliona dzikolo.+ 24 Koma chifukwa choti mtumiki wanga Kalebe+ anali wosiyana ndi ena,* ndipo wakhala akunditsatira ndi mtima wonse, ndithu ndidzamulowetsa mʼdziko limene anakalizonda, ndipo mbadwa zake zidzatenga dzikolo kukhala lawo.+ 25 Popeza Aamaleki ndi Akanani+ akukhala kuchigwa, mawa mubwerere nʼkuyamba ulendo wopita kuchipululu kudzera njira yopita ku Nyanja Yofiira.”+
26 Kenako Yehova anauza Mose ndi Aroni kuti: 27 “Kodi gulu la anthu oipa amenewa lingʼungʼudza motsutsana nane mpaka liti?+ Ndamva kungʼungʼudza kumene Aisiraeli akuchita motsutsana nane.+ 28 Uwauze kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Pali ine Mulungu wamoyo, ndidzakuchitirani mogwirizana ndi zimene ndamva mukulankhula.+ 29 Mitembo yanu idzagona mʼchipululu muno,+ nonsenu amene munawerengedwa, kuyambira azaka 20 kupita mʼtsogolo, inu amene mwakhala mukudandaula motsutsana nane.+ 30 Nonsenu simudzalowa mʼdziko limene ndinalumbira* kuti mudzakhalamo,+ kupatula Kalebe mwana wa Yefune ndi Yoswa mwana wa Nuni.+
31 Koma ana anu amene munati adzatengedwa ndi adani,+ amenewo ndi amene ndidzawalowetse mʼdzikolo ndipo adzadziwa dziko limene inu mwalikana.+ 32 Koma inuyo mitembo yanu idzagona mʼchipululu muno. 33 Ana anu adzakhala abusa mʼchipululu kwa zaka 40,+ ndipo adzavutika chifukwa cha kusakhulupirika kwanu,* mpaka womalizira kufa wa inu atagona mʼmanda mʼchipululu muno.+ 34 Mudzalangidwa mogwirizana ndi kuchuluka kwa masiku amene munazonda dzikolo, kwa masiku 40.+ Mudzalangidwa kwa zaka 40+ chifukwa cha zolakwa zanu, tsiku limodzi kuwerengera chaka chimodzi, tsiku limodzi chaka chimodzi, kuti mudziwe kuipa kotsutsana ndi ine.*
35 Ine Yehova ndalankhula. Zimene ndidzachitire gulu lonse la anthu oipali, amene asonkhana kuti atsutsane ndi ine ndi izi: Onse adzafera mʼchipululu muno ndipo adzathera momwe muno.+ 36 Komanso amuna amene Mose anawatuma kukazonda dzikolo, omwe anabweretsa lipoti loipa nʼkupangitsa kuti anthu onse adandaule motsutsana ndi Mose,+ 37 amuna amene anadzanena zoipa zokhazokha zokhudza dzikolo, Yehova adzawapatsa chilango ndipo adzafa.+ 38 Koma Yoswa mwana wa Nuni ndi Kalebe mwana wa Yefune, amene anali mʼgulu la anthu amene anakazonda dziko, adzakhalabe ndi moyo ndithu.”’”+
39 Mose atawauza Aisiraeli onse mawu amenewa, anthu onse anayamba kulira kwambiri. 40 Komanso, iwo anadzuka mʼmawa kwambiri kuti apite kudera lamapiri lija, ndipo anati: “Ife takonzeka kuti tipite kumalo amene Yehova ananena, chifukwa tachimwa.”+ 41 Koma Mose anati: “Nʼchifukwa chiyani mukuphwanya lamulo la Yehova? Zimenezo sizikuthandizani. 42 Musapite kumeneko chifukwa Yehova sali nanu ndipo adani anuwo akakugonjetsani.+ 43 Kumeneko mukakumana ndi Aamaleki komanso Akanani,+ ndipo akakuphani ndi lupanga. Yehova sapita nanu kumeneko chifukwa mwasiya kutsatira Yehova.”+
44 Komabe anthuwo anadzikuza ndipo ananyamuka nʼkupita kudera lamapiri kuja,+ koma Mose limodzi ndi likasa la pangano la Yehova sanachoke pakati pa msasa.+ 45 Zitatero Aamaleki ndi Akanani omwe ankakhala kudera lamapirilo anatsika nʼkuyamba kuwapha ndi kuwabalalitsa mpaka ku Horima.+
15 Yehova analankhulanso ndi Mose kuti: 2 “Lankhula ndi Aisiraeli ndipo uwauze kuti, ‘Mukakafika mʼdziko limene ndikukupatsani kuti muzikakhalamo,+ 3 ndipo mukamakapereka kwa Yehova nsembe yowotcha pamoto, kaya ndi ya ngʼombe kapena ya nkhosa, kuti ikhale nsembe yopsereza,+ kapena nsembe imene mukuipereka chifukwa cha lonjezo lapadera,+ kapena nsembe yaufulu, kapenanso nsembe imene mukupereka pa nthawi ya zikondwerero zanu,+ kuti ikhale kafungo kosangalatsa* kwa Yehova,+ 4 munthu amene akupereka nsembeyo, azikaperekanso kwa Yehova nsembe yambewu ya ufa wosalala+ wokwana gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa efa.* Ufawo uzikakhala wothira mafuta okwana gawo limodzi mwa magawo 4 a muyezo wa hini.* 5 Muzikaperekanso vinyo kuti akhale nsembe yachakumwa. Azikakhala wokwana gawo limodzi mwa magawo 4 a muyezo wa hini. Vinyoyo muzikamupereka limodzi ndi nsembe yopsereza,+ kapena ndi nsembe ya mwana wa nkhosa wamphongo. 6 Komanso popereka nsembe ya nkhosa yamphongo, muzikaipereka limodzi ndi nsembe yambewu yokwana magawo awiri a magawo 10 a ufa wosalala a muyezo wa efa. Ufawo uzikakhala wothira mafuta okwana gawo limodzi mwa magawo atatu a muyezo wa hini. 7 Ndiponso muzikapereka vinyo kuti akhale nsembe yachakumwa. Azikakhala wokwana gawo limodzi mwa magawo atatu a muyezo wa hini, kuti akhale nsembe yakafungo kosangalatsa* kwa Yehova.
8 Koma ngati mukupereka ngʼombe yamphongo kuti ikhale nsembe yopsereza,+ kapena nsembe imene mukuipereka chifukwa cha lonjezo lapadera,+ kapenanso kuti ikhale nsembe yamgwirizano kwa Yehova,+ 9 munthu amene akuperekayo azikapereka ngʼombe yamphongoyo limodzi ndi nsembe yambewu.+ Nsembe yambewuyo izikakhala yokwana magawo atatu a magawo 10 a ufa wosalala a muyezo wa efa. Ufawo azikauthira mafuta okwana hafu ya muyezo wa hini. 10 Ndiponso muzikapereka vinyo kuti akhale nsembe yachakumwa.+ Vinyoyo azikakhala wokwana hafu ya muyezo wa hini. Akakhale nsembe yowotcha pamoto, yakafungo kosangalatsa* kwa Yehova. 11 Izi nʼzimene mukuyenera kumakachita popereka ngʼombe yamphongo iliyonse, nkhosa yamphongo iliyonse, mwana wa nkhosa wamphongo aliyense kapena mbuzi iliyonse. 12 Muzikachita zimenezi ndi nyama iliyonse imene mukuipereka nsembe, ngakhale zitachuluka bwanji. 13 Munthu aliyense amene ndi nzika mu Isiraeli azikachita zimenezi popereka nsembe yowotcha pamoto, yakafungo kosangalatsa* kwa Yehova.
14 Ngati mlendo amene akukhala nanu kapena amene wakhala nanu kwa mibadwomibadwo, akufuna kupereka nsembe yowotcha pamoto yakafungo kosangalatsa* kwa Yehova, azikachita ngati mmene inu mukuchitira.+ 15 Inu amene ndinu mpingo wa Isiraeli komanso mlendo amene akukhala pakati panu, mukhale ndi malamulo ofanana. Muzitsatira malamulo amenewa mʼmibadwo yanu yonse mpaka kalekale, mlendo komanso inuyo nʼchimodzimodzi pamaso pa Yehova.+ 16 Pakhale malamulo ndi zigamulo zofanana kwa inu ndi kwa alendo amene akukhala nanu.’”
17 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 18 “Lankhula ndi Aisiraeli ndipo uwauze kuti, ‘Mukakalowa mʼdziko limene ndikukupititsani, 19 muzikapereka chopereka kwa Yehova pa chakudya chilichonse chamʼdzikolo,+ chimene muzikadya. 20 Muzikapereka mikate yozungulira yoboola pakati ya ufa wamisere kuti ikhale chopereka cha zipatso zoyambirira kucha.+ Muzikaipereka ngati mmene mumaperekera chopereka chochokera popunthira mbewu. 21 Muzikapereka kwa Yehova ufa wamisere wa zina mwa zipatso zanu zoyambirira ku mibadwo yanu yonse.
22 Koma mukalakwitsa zinthu nʼkulephera kusunga malamulo onsewa amene Yehova walankhula kudzera mwa Mose, 23 zonse zimene Yehova wakulamulani kudzera mwa Mose, kuchokera pa tsiku limene Yehova analamula mpaka mʼtsogolo mʼmibadwo yanu yonse, 24 ngati mwalakwitsa mosazindikira, ndipo gulu lonselo silinadziwe, gulu lonselo lizikapereka ngʼombe yaingʼono yamphongo kuti ikhale nsembe yopsereza yakafungo kosangalatsa* kwa Yehova. Muzikapereka nsembeyo limodzi ndi nsembe yake yambewu ndiponso nsembe yake yachakumwa potsatira dongosolo la nthawi zonse.+ Muzikaperekanso mbuzi yaingʼono imodzi kuti ikhale nsembe yamachimo.+ 25 Wansembe azikapereka nsembe yophimba machimo a gulu lonse la Aisiraeli. Akatero, anthuwo adzakhululukidwa+ chifukwa analakwitsa mosazindikira, komanso chifukwa apereka nsembe yopsereza kwa Yehova ndiponso apereka nsembe yamachimo kwa Yehova chifukwa cha zimene analakwitsazo. 26 Gulu lonse la Aisiraeli lidzakhululukidwa limodzi ndi mlendo amene akukhala nawo, chifukwa anthu onsewo analakwitsa zinthu mosazindikira.
27 Munthu aliyense akachimwa mosazindikira, azidzapereka mbuzi yaikazi yosapitirira chaka chimodzi kuti ikhale nsembe yamachimo.+ 28 Wansembe azidzapereka nsembe yophimba tchimo la munthu amene walakwa pochimwira Yehova mosazindikira, ndipo adzakhululukidwa.+ 29 Munthu akachita tchimo mosazindikira,+ padzakhale lamulo lofanana kwa munthu amene ndi nzika mu Isiraeli ndi kwa mlendo wokhala pakati pawo.
30 Koma munthu amene wachita tchimo mwadala,+ kaya akhale nzika kapena mlendo, ndiye kuti wanyoza Yehova ndipo ayenera kuphedwa kuti asakhalenso pakati pa anthu ake. 31 Chifukwa chakuti wanyoza mawu a Yehova komanso waphwanya lamulo lake, munthuyo aziphedwa ndithu.+ Aziyankha mlandu wa tchimo lakelo.’”+
32 Aisiraeli ali mʼchipululumo, tsiku lina anapeza munthu wina akutola nkhuni pa tsiku la Sabata.+ 33 Amene anamupeza akutola nkhuniwo anapita naye kwa Mose ndi Aroni ndiponso kumene kunali gulu lonselo. 34 Iwo anamutsekera+ chifukwa panalibe lamulo lachindunji la zimene ayenera kuchita ndi munthuyo.
35 Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti: “Munthuyo aphedwe basi.+ Gulu lonse likamuponye miyala kunja kwa msasa.”+ 36 Choncho gulu lonselo linapita naye kunja kwa msasa kumene linakamuponya miyala mpaka kufa, mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose.
37 Yehova anauzanso Mose kuti: 38 “Lankhula ndi Aisiraeli ndipo uwauze kuti azisokerera ulusi mʼmphepete mwa zovala zawo, ku mibadwo yawo yonse. Azisokereranso chingwe cha buluu pamwamba pa ulusi wa mphepete mwa zovalazo.+ 39 ‘Zovala zanu zizikhala ndi ulusi kuti mukaziona muzikumbukira malamulo onse a Yehova ndi kuwasunga.+ Musamatsatire zilakolako za mitima yanu ndi maso anu, chifukwa nʼzimene zikukupangitsani kuti musakhale okhulupirika kwa ine.*+ 40 Lamulo limeneli likuthandizani kuti muzikumbukira komanso kusunga malamulo anga onse ndiponso kukhala oyera kwa Mulungu wanu.+ 41 Ine ndine Yehova Mulungu wanu,+ amene ndinakutulutsani mʼdziko la Iguputo, kuti ndisonyeze kuti ndine Mulungu wanu. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.’”+
16 Kenako Kora+ mwana wa Izara,+ mwana wa Kohati,+ mwana wa Levi,+ anagwirizana ndi adzukulu a Rubeni,+ omwe ndi Datani ndi Abiramu ana a Eliyabu,+ komanso Oni mwana wa Pelete, kuti aukire. 2 Iwo limodzi ndi amuna a Chiisiraeli okwana 250 anaukira Mose. Amunawa anali atsogoleri a anthuwo, amuna osankhidwa pakati pa Aisiraeli, amuna otchuka. 3 Choncho iwo anasonkhana nʼkuyamba kutsutsana+ ndi Mose ndi Aroni kuti: “Tatopa nanu tsopano. Gulu lonseli ndi loyera,+ ndipo Yehova ali pakati pawo.+ Nanga nʼchifukwa chiyani inu mukudzikweza pa mpingo wa Yehova?”
4 Mose atamva zimenezi, nthawi yomweyo anagwada nʼkuwerama mpaka nkhope yake pansi. 5 Ndiyeno Mose anauza Kora ndi anthu onse amene ankamutsatira kuti: “Mawa mʼmamawa, Yehova adzasonyeza munthu amene ali wake+ ndiponso amene ali woyera, amene ali woyenera kuyandikira pamaso pake.+ Ndipo amene ati adzamusankheyo+ adzayandikira pamaso pake. 6 Mudzachite izi: Iweyo Kora ndi anthu onse amene akukutsatira+ mudzatenge zofukizira.+ 7 Mʼzofukizirazo mudzaikemo moto komanso zofukiza nʼkubwera nazo pamaso pa Yehova mawa. Munthu amene Yehova adzamusankhe,+ ndi amene ali woyera. Inu ana a Levi+ mwawonjeza kwambiri.”
8 Ndiyeno Mose anauza Kora kuti: “Tamverani, inu ana a Levi. 9 Kodi mukuyesa nʼchinthu chachingʼono kuti Mulungu wa Isiraeli anakupatulani pakati pa Aisiraeli,+ nʼkukulolani kuti muzifika pamaso pa Yehova kuti muzimutumikira pachihema chake komanso kutumikira gulu lonselo?+ 10 Kodi ndi chinthu chachingʼono kuti Mulungu anakubweretsani pafupi ndi iye limodzi ndi abale anu onse, ana a Levi? Kodi tsopano mukufunanso udindo waunsembe?+ 11 Chifukwa cha zimene mukuchitazi, iweyo limodzi ndi anthu onse amene akukutsatira, mukuukira Yehova. Kunena za Aroni, kodi iyeyo ndi ndani kuti mumudandaule?”+
12 Pambuyo pake, Mose anatuma munthu kuti akaitane Datani ndi Abiramu,+ ana a Eliyabu. Koma iwo anayankha kuti: “Ife sitibwerako kumeneko! 13 Kodi ukuyesa nʼchinthu chachingʼono kuti unatichotsa mʼdziko loyenda mkaka ndi uchi kuti udzatiphere mʼchipululu muno?+ Kodi tsopano ukufunanso kuti ukhale mfumu yomatilamulira? 14 Si izi nanga, sunatifikitse kudziko lililonse loyenda mkaka ndi uchi+ kapena kutipatsa malo ndiponso minda ya mpesa. Kodi ukufuna kuti amunawo uwakolowole maso? Tatitu kumeneko sitibwerako!”
15 Mose atamva zimenezi anakwiya kwambiri ndipo anauza Yehova kuti: “Nsembe zawo zambewu musaziyangʼane. Ine sindinawalande ngakhale bulu mmodzi, kapena kuchitira aliyense wa anthuwo chinthu choipa.”+
16 Kenako Mose anauza Kora kuti: “Mawa, iweyo ndi anthu onse amene akukutsatira mukaonekere pamaso pa Yehova. Mukaonekere, iweyo, anthuwo komanso Aroni. 17 Aliyense adzatenge chofukizira chake nʼkuikamo zofukiza, ndipo aliyense adzabweretse chofukizira chake pamaso pa Yehova. Zofukizirazo zidzakhale zokwana 250, komanso iweyo ndi Aroni aliyense adzakhale ndi chake.” 18 Choncho aliyense wa iwo anatenga chofukizira chake nʼkuikamo moto ndi zofukiza. Atatero, anakaima pakhomo la chihema chokumanako limodzi ndi Mose ndi Aroni. 19 Kora atasonkhanitsa anthu onse omutsatira+ kuti atsutsane nawo pakhomo la chihema chokumanako, ulemerero wa Yehova unaonekera ku gulu lonselo.+
20 Tsopano Yehova anauza Mose ndi Aroni kuti: 21 “Chokani pakati pa gululi, kuti ndiwawononge kamodzinʼkamodzi.”+ 22 Anthuwo atamva zimenezi anagwada nʼkuwerama mpaka nkhope zawo pansi, nʼkunena kuti: “Chonde Mulungu, inu Mulungu amene amapereka moyo kwa anthu onse,*+ kodi mukupsera mtima gulu lonseli+ chifukwa cha kuchimwa kwa munthu mmodzi yekha?”
23 Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti: 24 “Uza gulu lonselo kuti, ‘Musayandikire matenti a Kora, Datani ndi Abiramu!’”+
25 Kenako Mose ananyamuka nʼkupita kwa Datani ndi Abiramu, ndipo akulu+ a Isiraeli anapita naye limodzi. 26 Atafika anauza gululo kuti: “Chonde, chokani kumatenti a anthu oipawa, ndipo musakhudze chinthu chawo chilichonse, kuti musaphedwe nawo limodzi chifukwa cha tchimo lawo.” 27 Nthawi yomweyo anthuwo anachoka kumbali zonse za matenti a Kora, Datani ndi Abiramu. Zitatero, Datani ndi Abiramu anatuluka nʼkuima pamakomo a matenti awo, limodzi ndi akazi awo, ana awo aamuna komanso ana awo angʼonoangʼono.
28 Ndiyeno Mose anati: “Mudziwira izi kuti Yehova ndi amene wandituma kuti ndichite zonsezi, ndiponso kuti si zamʼmaganizo mwanga:* 29 Ngati anthuwa angafe mmene anthu onse amafera, ndiponso ngati chilango chawo chingakhale chofanana ndi chimene anthu onse amapatsidwa, ndiye kuti Yehova sananditume.+ 30 Koma ngati Yehova angawachitire chinthu chachilendo, kuti nthaka ingʼambike* nʼkuwameza ndi zonse zimene ali nazo, moti iwo nʼkutsikira ku Manda* ali amoyo, zikatero mudziwa ndithu kuti amunawa anyoza Yehova.”
31 Mose atangomaliza kulankhula mawu amenewa, nthaka imene iwo anapondapo inangʼambika.+ 32 Nthakayo inangʼambika* nʼkuwameza limodzi ndi mabanja awo komanso anthu ena onse amene anali kumbali ya Kora+ pamodzi ndi katundu wawo yense. 33 Choncho iwo pamodzi ndi onse amene anali kumbali yawo analowa mʼManda* ali amoyo. Nthaka inawakwirira, moti iwo anawonongedwa pakati pa mpingo wonse.+ 34 Aisiraeli onse amene anali pamalopo anayamba kuthawa atamva kufuula kwawo, ndipo anati: “Tikuopa kuti nthaka ingatimeze!” 35 Kenako moto unachokera kwa Yehova+ ndipo unapsereza amuna 250 omwe ankapereka nsembe zofukiza aja.+
36 Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti: 37 “Uza Eleazara, mwana wa wansembe Aroni, kuti achotse pamoto zofukizirazo+ chifukwa nʼzopatulika. Umuuzenso kuti amwaze motowo kutali. 38 Zofukizira za amuna amene anafa chifukwa cha kuchimwa kwawo azisule kuti zikhale timalata topyapyala ndipo mukutire guwa lansembe.+ Zofukizirazo zinakhala zopatulika chifukwa anafika nazo pamaso pa Yehova. Ndiye timalatato tikhale chikumbutso kwa Aisiraeli.”+ 39 Choncho wansembe Eleazara anatenga zofukizira zakopa zimene anthu amene anapsa ndi moto aja anabweretsa, ndipo anazisula nʼkupanga timalata tokutira guwa lansembe, 40 mogwirizana ndi zimene Yehova anamuuza kudzera mwa Mose. Timalatato tinali chikumbutso kwa Aisiraeli kuti munthu wamba* amene si mbadwa ya Aroni asayandikire kwa Yehova kuti akapereke nsembe zofukiza.+ Anachita zimenezi kuti pasapezeke wina aliyense wochita zimene Kora limodzi ndi anthu amene ankamutsatira anachita.+
41 Koma tsiku lotsatira, gulu lonse la Aisiraeli linayamba kungʼungʼudza motsutsana ndi Mose komanso Aroni+ kuti: “Mwapha anthu a Yehova inu.” 42 Anthuwo anasonkhana pamodzi kuti aukire Mose ndi Aroni, kenako anatembenuka nʼkuyangʼana kuchihema chokumanako. Atatero anangoona kuti mtambo waphimba chihemacho ndipo ulemerero wa Yehova wayamba kuonekera.+
43 Ndiyeno Mose ndi Aroni anakaima patsogolo pa chihema chokumanako,+ 44 ndipo Yehova anauza Mose kuti: 45 “Amuna inu, chokani pakati pa anthuwa kuti ndiwawononge kamodzinʼkamodzi.”+ Atamva zimenezi, iwo anagwada nʼkuwerama mpaka nkhope zawo pansi.+ 46 Kenako Mose anauza Aroni kuti: “Tenga chofukizira ndipo uikemo moto wochokera paguwa lansembe.+ Uikemonso nsembe yofukiza nʼkupita kwa anthuwo mofulumira kuti ukawaphimbire machimo awo.+ Chita zimenezi chifukwa Yehova wakwiya kwambiri ndipo mliri wayamba kale!” 47 Nthawi yomweyo Aroni anatenga chofukiziracho mogwirizana ndi zimene Mose anamuuza, nʼkuthamanga kukalowa pakati pa mpingowo. Koma mliri unali utayamba kale pakati pawo. Choncho Aroni anaika nsembe yofukiza ija pachofukiziracho nʼkuyamba kuphimbira anthuwo machimo. 48 Aroni anaimabe pakati pa akufa ndi amoyo, ndipo patapita nthawi mliriwo unaleka. 49 Amene anafa ndi mliriwo anakwana 14,700, osawerengera amene anafa chifukwa cha zochita za Kora aja. 50 Pa nthawi imene Aroni ankabwerera kwa Mose pakhomo la chihema chokumanako, mliriwo unali utaleka.
17 Tsopano Yehova anauza Mose kuti: 2 “Lankhula ndi Aisiraeli, ndipo utenge ndodo imodzi kuchokera ku fuko lililonse, kwa mtsogoleri wa fukolo.+ Zikhalepo ndodo 12 ndipo ulembe dzina la mtsogoleri aliyense pa ndodo yake. 3 Pandodo ya fuko la Levi ulembepo dzina la Aroni, chifukwa ndodo iliyonse ikuimira mtsogoleri wa fuko. 4 Ndodozo uziike mʼchihema chokumanako, patsogolo pa Umboni,+ pamene ndimakumana nawe nthawi zonse.+ 5 Ndodo ya munthu amene ndimusankheyo+ idzaphuka, ndipo ndidzathetsa kungʼungʼudza kwa Aisiraeli kumene akuchita motsutsana ndi ine+ komanso motsutsana ndi iwe.”+
6 Choncho Mose analankhula ndi Aisiraeli ndipo atsogoleri awo onse anapereka ndodo zawo. Mtsogoleri aliyense anapereka ndodo imodzi ya fuko lake. Panali ndodo 12, ndipo imodzi inali ya Aroni. 7 Ndiyeno Mose anakaika ndodozo pamaso pa Yehova mʼchihema cha Umboni.
8 Tsiku lotsatira, Mose atalowa mʼchihema cha Umbonicho, anangoona kuti ndodo ya Aroni yoimira nyumba ya Levi yaphuka. Ndodoyo inali itaphuka ndipo inkamasula maluwa komanso kubereka zipatso za amondi zakupsa. 9 Kenako Mose anatenga ndodo zonse pamaso pa Yehova nʼkupita nazo kwa Aisiraeli onse. Atsogoleri aja anayangʼana ndodozo, ndipo aliyense anatengapo yake.
10 Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti: “Bwezera ndodo ya Aroni+ patsogolo pa Umboni. Uisunge kuti ikhale chikumbutso+ kwa ana opandukawa,+ nʼcholinga chakuti asiye kungʼungʼudza motsutsana ndi ine komanso kuti asafe.” 11 Nthawi yomweyo Mose anachita mogwirizana ndi zimene Yehova anamulamula. Anachitadi zomwezo.
12 Ndiyeno Aisiraeli anauza Mose kuti: “Tsopano ife tifa. Ndithudi titha ife. Tonse titha basi. 13 Aliyense amene ayerekeze kuyandikira chihema cha Yehova afa.+ Koma zoona ife tife mwa njira imeneyi?”+
18 Kenako Yehova anauza Aroni kuti: “Iwe ndi ana ako, ndi nyumba yonse ya bambo ako, mudzayankha mlandu wa zolakwa zanu pa malamulo okhudza malo opatulika.+ Iweyo ndi ana ako mudzayankha mlandu wa zolakwa zanu pa malamulo okhudza unsembe wanu.+ 2 Utengenso abale ako a fuko la Levi, omwe ndi a mtundu wa bambo ako, kuti azikuthandiza. Azitumikira iweyo+ limodzi ndi ana ako pachihema cha Umboni.+ 3 Azichita utumiki umene mwawapatsa komanso azigwira ntchito zawo zonse zapachihema.+ Koma asamayandikire zipangizo zamʼmalo oyera, kapena kuyandikira guwa lansembe kuti iwowo kapena inuyo musafe.+ 4 Azikuthandizani komanso azigwira ntchito zawo zonse zapachihema chokumanako, ndipo munthu wamba* aliyense asamayandikire kwa inu.+ 5 Inu nokha ndi amene muzigwira ntchito za ansembe mʼmalo opatulika+ ndi paguwa lansembe,+ kuti ndisadzakwiyirenso+ Aisiraeli. 6 Ine ndatenga Alevi omwe ndi abale anu pakati pa Aisiraeli ndipo ndawapereka kwa inu kuti akhale mphatso yanu.+ Iwo aperekedwa kwa Yehova kuti azitumikira pachihema chokumanako.+ 7 Iweyo ndi ana ako, udindo wanu ndi kugwira ntchito zaunsembe paguwa lansembe komanso pa zinthu zamkati ndi kuseri kwa katani.+ Umenewu ndi utumiki wanu.+ Ndakupatsani utumiki waunsembe kuti ukhale mphatso kwa inu, ndipo munthu wamba* aliyense akayandikira pafupi aziphedwa.”+
8 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Aroni kuti: “Ine ndakupatsa udindo woyangʼanira zinthu zonse zimene anthu azipereka kwa ine.+ Pa zinthu zonse zopatulika zimene Aisiraeli azipereka, ndakupatsa gawo iweyo ndi ana ako, kuti likhale lanu mpaka kalekale.+ 9 Gawo limene muzilandira lizichokera pa nsembe zonse zopatulika koposa zowotcha pamoto. Nsembe zake ndi izi: nsembe zilizonse zimene angapereke kwa ine, kuphatikizapo nsembe zawo zambewu,+ nsembe zawo zamachimo+ komanso nsembe zawo zakupalamula.+ Gawolo lizikhala chinthu chopatulika koposa kwa iwe ndi ana ako. 10 Uzilidyera mʼmalo oyera koposa,+ ndipo mwamuna aliyense wa fuko lanu angathe kudya nawo. Gawo limenelo lizikhala chinthu chopatulika kwa iwe.+ 11 Zinthu izinso zizikhala zako: mphatso zonse za Aisiraeli,+ limodzi ndi nsembe zawo zonse zoyendetsa uku ndi uku+ zimene azipereka. Ndazipereka kwa iwe ndi kwa ana ako aamuna komanso ana ako aakazi kuti zikhale gawo lanu mpaka kalekale.+ Aliyense wamʼnyumba yako amene si wodetsedwa angathe kudya nawo.+
12 Ndakupatsa+ mafuta onse abwino koposa, vinyo yense watsopano wabwino koposa ndi mbewu zabwino koposa, zimenezi ndi zipatso zawo zoyambirira+ zimene azipereka kwa Yehova. 13 Zipatso zonse zoyamba kupsa mʼminda yawo, zimene azizipereka kwa Yehova zizikhala zako.+ Aliyense wamʼnyumba yako amene si wodetsedwa angathe kudya nawo.
14 Chinthu chilichonse chimene anthu achipereka kwa Mulungu* mu Isiraeli chizikhala chako.+
15 Chamoyo chilichonse choyamba kubadwa+ chimene azipereka kwa Yehova, kaya ndi munthu kapena nyama, chizikhala chako. Komabe uzionetsetsa kuti wawombola mwana woyamba kubadwa wa munthu+ komanso mwana woyamba kubadwa wa nyama yodetsedwa.+ 16 Mwanayo akakwanitsa mwezi umodzi kapena kuposerapo uzimuwombola ndi mtengo wowombolera. Uzimuwombola pa mtengo umene anaikiratu wa masekeli asiliva 5,*+ mogwirizana ndi sekeli lakumalo oyera* lomwe ndi lokwana magera 20.* 17 Koma usawombole ngʼombe yamphongo yoyamba kubadwa, mwana wa nkhosa wamphongo woyamba kubadwa, kapena mbuzi yoyamba kubadwa.+ Zimenezi ndi zopatulika. Magazi ake uziwawaza paguwa lansembe,+ ndipo mafuta ake uziwawotcha pamoto kuti akhale nsembe yakafungo kosangalatsa* kwa Yehova.+ 18 Uzitenga nyama yake kuti ikhale yako. Ngati mmene umachitira ndi chidale cha nsembe yoyendetsa uku ndi uku komanso mwendo wamʼmbuyo wakumanja, nyamayi izikhala yako.+ 19 Zopereka zonse zopatulika zimene Aisiraeli azipereka kwa Yehova,+ ndakupatsa iwe ndi ana ako aamuna ndi aakazi, kuti likhale gawo lanu mpaka kalekale.+ Limeneli ndi pangano lamuyaya lamchere* limene Yehova akupanga ndi iwe komanso mbadwa zako.”
20 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Aroni kuti: “Iwe udzakhala wopanda cholowa mʼdziko mwawo, ndipo sudzapatsidwa malo pakati pawo kuti akhale cholowa chako.+ Ine ndine gawo lako ndi cholowa chako pakati pa Aisiraeli.+
21 Ine ndapereka kwa ana a Levi chakhumi chilichonse+ mu Isiraeli kuti chikhale cholowa chawo chifukwa cha utumiki umene akuchita, utumiki wapachihema chokumanako. 22 Aisiraeli asadzayandikirenso chihema chokumanako, chifukwa akadzatero adzachimwa nʼkufa. 23 Aleviwo azichita utumiki wawo pachihema chokumanako, ndipo ndi amene aziyankha mlandu wa zolakwa za anthuwo.+ Iwo asakhale ndi cholowa pakati pa Aisiraeli.+ Limeneli ndi lamulo mpaka kalekale mʼmibadwo yanu yonse. 24 Chakhumi chimene Aisiraeli azipereka kwa Yehova, ndapereka kwa Alevi kuti chikhale cholowa chawo. Nʼchifukwa chake ndinawauza kuti, ‘Asalandire cholowa pakati pa Aisiraeli.’”+
25 Kenako Yehova anauza Mose kuti: 26 “Uza Alevi kuti, ‘Muzilandira kwa Aisiraeli chakhumi chimene ndakupatsani kuti chikhale cholowa chanu.+ Ndipo pa chakhumi chimene muzilandiracho, muzipereka chakhumi kwa Yehova.+ 27 Chakhumicho Mulungu azichiona kuti ndi chopereka chanu mofanana ndi tirigu wochokera pamalo opunthira,+ vinyo wochuluka wochokera mopondera mphesa kapena mafuta ochuluka ochokera mʼchofinyira mafuta. 28 Mukamachita zimenezi inunso muzikhala kuti mwapereka chopereka chanu kwa Yehova, kuchokera pa zakhumi zonse zimene muzilandira kuchokera kwa Aisiraeli. Kuchokera pa zakhumizo, muzipereka chopereka chanu kwa Yehova popereka kwa Aroni wansembe. 29 Pa mphatso zonse zabwino koposa zimene mwalandira monga chinthu chopatulika, muzipereka kwa Yehova zopereka zosiyanasiyana.’+
30 Ndipo uwauze kuti, ‘Mukapereka zabwino koposa za zoperekazo, Mulungu aziona kuti Alevinu mwapereka tirigu wochokera pamalo opunthira, vinyo wochokera mopondera mphesa kapena mafuta ochokera mʼchofinyira mafuta. 31 Inuyo ndi amʼnyumba mwanu muzidya zimenezo pamalo alionse, chifukwa amenewo ndi malipiro anu pa utumiki umene muzichita pachihema chokumanako.+ 32 Mukapereka zinthu zabwino koposa kuchokera pa zinthu zimenezi, simudzachimwa ngati mutadya, komanso musaipitse zinthu zopatulika za Aisiraeli, kuti musafe.’”+
19 Yehova analankhulanso ndi Mose komanso Aroni kuti: 2 “Ili ndi lamulo limene Yehova wapereka, ‘Uzani Aisiraeli kuti akupatseni ngʼombe yaikazi yofiira, yathanzi komanso yopanda chilema+ yomwe sinamangidwepo goli. 3 Mupereke ngʼombeyo kwa wansembe Eleazara kuti apite nayo kunja kwa msasa, ndipo kumeneko ikaphedwe pamaso pake. 4 Akatero wansembe Eleazara atenge ena mwa magazi a ngʼombeyo ndi chala chake nʼkuwawaza chakutsogolo kwa chihema chokumanako maulendo 7.+ 5 Kenako ngʼombeyo iwotchedwe iyeyo akuona. Awotche chikopa chake, nyama yake, magazi ake, limodzi ndi ndowe zake.+ 6 Wansembeyo atenge mtengo wa mkungudza, kamtengo ka hisope+ ndi ulusi wofiira kwambiri nʼkuziponya pamoto umene akuwotcherapo ngʼombeyo. 7 Akatha, wansembeyo achape zovala zake nʼkusamba* ndi madzi. Pambuyo pake akhoza kulowa mumsasa, koma adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo.
8 Munthu amene anawotcha ngʼombeyo achape zovala zake nʼkusamba* ndi madzi, ndipo adzakhala wodetsedwa mpaka madzulo.
9 Ndiyeno munthu amene si wodetsedwa awole phulusa la ngʼombeyo+ nʼkukalisiya pamalo oyera kunja kwa msasawo. Aisiraeli onse azisunga phulusalo kuti aziligwiritsa ntchito pokonza madzi oyeretsera.+ Imeneyi ndi nsembe yamachimo. 10 Munthu amene wawola phulusa la ngʼombeyo azichapa zovala zake ndipo azikhala wodetsedwa mpaka madzulo.
Limeneli ndi lamulo mpaka kalekale kwa Aisiraeli komanso kwa mlendo wokhala pakati pawo.+ 11 Aliyense wokhudza mtembo wa munthu aliyense, azikhala wodetsedwa kwa masiku 7.+ 12 Munthu woteroyo azidziyeretsa ndi madzi oyeretsera aja pa tsiku lachitatu, ndipo pa tsiku la 7 azikhala woyera. Koma akapanda kudziyeretsa pa tsiku lachitatu, sadzakhala woyera pa tsiku la 7. 13 Munthu aliyense amene wakhudza mtembo wa munthu, koma sanadziyeretse, wadetsa chihema cha Yehova.+ Munthu ameneyo aziphedwa kuti asakhalenso pakati pa Isiraeli.+ Iye adakali wodetsedwa chifukwa sanawazidwe madzi oyeretsera.+ Choncho adzakhalabe wodetsedwa.
14 Ngati munthu wafera mutenti, lamulo lake ndi ili: Munthu aliyense amene walowa mutentimo komanso aliyense amene anali mutenti momwemo, adzakhala wodetsedwa kwa masiku 7. 15 Chiwiya chilichonse chosavundikira bwino* ndi chodetsedwa.+ 16 Aliyense amene wakhudza munthu amene waphedwa ndi lupanga kunja kwa msasa, kapena mtembo, fupa la munthu, kapenanso manda, adzakhala wodetsedwa kwa masiku 7.+ 17 Munthu wodetsedwayo amutapireko phulusa la nsembe yamachimo imene inawotchedwa ija. Phulusalo aliike mʼchiwiya nʼkuthiramo madzi akumtsinje. 18 Ndiyeno munthu amene si wodetsedwa+ azitenga kamtengo ka hisope+ nʼkukaviika mʼmadzimo kenako aziwaza tentiyo, ziwiya zonse ndi anthu onse amene anali mutentiyo. Komanso aziwaza munthu amene anakhudza fupa la munthu, munthu amene waphedwa, mtembo kapena manda. 19 Munthu amene si wodetsedwa uja awaze munthu wodetsedwayo madziwo pa tsiku lachitatu komanso pa tsiku la 7.+ Ndipo pa tsiku la 7 lomwelo amuyeretse ku tchimo lake. Kenako amene akuyeretsedwayo achape zovala zake nʼkusamba ndi madzi, ndipo madzulo ake adzakhala woyera.
20 Koma munthu wodetsedwa akapanda kudziyeretsa, aziphedwa kuti asakhalenso mumpingowo,+ chifukwa wadetsa malo opatulika a Yehova. Iye sanawazidwe madzi oyeretsera, choncho ndi wodetsedwa.
21 Limeneli likhale lamulo kwa iwo mpaka kalekale: Munthu amene anawaza madzi oyeretsera,+ azichapa zovala zake. Ndipo munthu amene angakhudze madzi oyeretserawo azikhala wodetsedwa mpaka madzulo. 22 Chinthu chilichonse chimene munthu wodetsedwayo angakhudze, chizikhala chodetsedwa. Komanso munthu amene angakhudze chinthucho, azikhala wodetsedwa mpaka madzulo.’”+
20 Mʼmwezi woyamba, gulu lonse la Aisiraeli linafika mʼchipululu cha Zini, ndipo anthuwo anakhala ku Kadesi.+ Kumeneko nʼkumene Miriamu+ anafera nʼkuikidwa mʼmanda.
2 Koma anthuwo anasowa madzi pamalopo,+ ndipo anasonkhana nʼkuukira Mose ndi Aroni. 3 Anthuwo anayamba kukangana ndi Mose+ kuti: “Zikanakhala bwino tikanangofera limodzi ndi abale athu aja amene anafa pamaso pa Yehova. 4 Nʼchifukwa chiyani mwabweretsa mpingo wa Yehova kuchipululu kuno kuti ife limodzi ndi ziweto zathu tifere kuno?+ 5 Nʼchifukwa chiyani munatitulutsa mʼdziko la Iguputo nʼkutibweretsa kumalo oipa ano?+ Kuno sikungamere mbewu iliyonse ndipo kulibe mitengo ya nkuyu, mitengo ya mpesa kapena mitengo ya makangaza. Ndi madzi akumwa omwe kulibe.”+ 6 Zitatero Mose ndi Aroni anachoka pamaso pa mpingowo nʼkupita kukhomo la chihema chokumanako. Kumeneko, anagwada nʼkuwerama mpaka nkhope zawo pansi, ndipo ulemerero wa Yehova unayamba kuonekera kwa iwo.+
7 Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti: 8 “Tenga ndodo ndipo iweyo ndi mʼbale wako Aroni, musonkhanitse gulu lonse la anthuwo. Muuze thanthwe pamaso pawo kuti litulutse madzi. Utulutse madzi mʼthanthweli kuti upatse gululo, kuti limwe limodzi ndi ziweto zawo.”+
9 Choncho Mose anatenga ndodo ija pamaso pa Yehova+ mogwirizana ndi zimene anamulamula. 10 Kenako Mose ndi Aroni anasonkhanitsa mpingo wonse pamodzi patsogolo pa thanthwelo, ndipo Mose anawauza kuti: “Tsopano tamverani anthu opanduka inu! Kodi tikutulutsireni madzi mʼthanthweli?”+ 11 Mose atatero, anakweza dzanja lake nʼkumenya thanthwelo kawiri ndi ndodo yake. Ndiyeno madzi ambiri anayamba kutuluka ndipo gulu lonselo linayamba kumwa madziwo limodzi ndi ziweto zawo.+
12 Pambuyo pake Yehova anauza Mose ndi Aroni kuti: “Chifukwa simunasonyeze chikhulupiriro mwa ine ndipo simunandilemekeze pamaso pa Aisiraeli, simudzalowetsa mpingowu mʼdziko limene ndidzawapatse.”+ 13 Madzi amenewo anatchedwa madzi a ku Meriba,*+ kumene Aisiraeli anakangana ndi Yehova ndipo anawasonyeza kuti iye ndi woyera.
14 Kenako Mose anatumiza anthu kuchokera ku Kadesi kupita kwa mfumu ya Edomu+ kukanena kuti: “Abale anu Aisiraeli+ akuti, ‘Inu mukudziwa bwino za mavuto onse amene takumana nawo. 15 Paja makolo athu anapita ku Iguputo+ ndipo tinakhala kumeneko zaka zambiri.*+ Aiguputowo ankatizunza ifeyo limodzi ndi makolo athu.+ 16 Potsirizira pake, tinalirira Yehova+ ndipo iye anamva kulira kwathu. Iye anatitumizira mngelo+ nʼkutitulutsa mʼdziko la Iguputo. Tsopano tili kuno ku Kadesi, mzinda umene uli mʼmalire a dziko lanu. 17 Chonde mutilole tidutse mʼdziko lanu. Sitidutsa mʼmunda wanu uliwonse, kapena mʼmunda wa mpesa uliwonse. Sitimwa madzi apachitsime chanu chilichonse. Tizingoyenda mu Msewu wa Mfumu, osakhotera kudzanja lamanja kapena lamanzere, mpaka titadutsa mʼdziko lanu.’”+
18 Koma mfumu ya Edomu inawayankha kuti: “Musadzere mʼdziko lathu. Mukadzera, ndibwera ndi lupanga kudzamenyana nanu.” 19 Aisiraeliwo anayankha kuti: “Ife tidzangodutsa mumsewu waukulu, ndipo ngati ifeyo kapena ziweto zathu tingamwe madzi anu, tidzakulipirani.+ Sitikufuna chilichonse ayi, koma kungodutsa mʼdziko lanu basi.”+ 20 Koma iye anakanabe kuti: “Ayi, musadzere mʼdziko lathu.”+ Mfumu ya Edomu itanena zimenezi, inatuluka ndi chigulu cha anthu komanso asilikali amphamvu.* 21 Choncho mfumu ya Edomu inakana kulola Aisiraeli kudzera mʼdziko lake. Zitatero, Aisiraeli analambalala dziko la Edomu.+
22 Gulu lonse la Aisiraeli linanyamuka ku Kadesi kuja nʼkukafika kuphiri la Hora.+ 23 Kenako Yehova anauza Mose ndi Aroni mʼphiri la Hora, mʼmalire a dziko la Edomu kuti: 24 “Aroni aikidwa mʼmanda ngati mmene zinakhalira ndi makolo ake.*+ Iye sadzalowa mʼdziko limene ndidzapatse Aisiraeli chifukwa awirinu munapandukira malangizo anga okhudza madzi a ku Meriba.+ 25 Utenge Aroni ndi mwana wake Eleazara nʼkukwera nawo phiri la Hora. 26 Mʼphirimo, ukamuvule Aroni zovala zake zaunsembe,+ nʼkuveka mwana wake Eleazara+ ndipo Aroni akamwalira kumeneko.”
27 Choncho Mose anachitadi zimene Yehova anamulamula. Iwo anakwera mʼphiri la Hora anthu onsewo akuona. 28 Kumeneko, Mose anavula Aroni zovala zake zaunsembe nʼkuveka mwana wake Eleazara. Pambuyo pake, Aroni anamwalira pamwamba pa phiripo.+ Potsirizira pake, Mose ndi Eleazara anatsika mʼphirimo. 29 Gulu lonse la anthuwo litaona kuti Aroni wamwalira, nyumba yonse ya Isiraeli inalira maliro a Aroni kwa masiku 30.+
21 Mfumu ya Akanani ya ku Aradi+ yomwe inkakhala ku Negebu itamva kuti Aisiraeli akubwera kudzera njira ya ku Atarimu, inapita kukamenyana nawo ndipo inagwira Aisiraeli ena nʼkupita nawo kudziko lake. 2 Aisiraeli ataona zimenezo, analonjeza Yehova kuti: “Mukapereka anthuwa mʼmanja mwathu, ndithu ifenso tidzawononga mizinda yawo.” 3 Choncho Yehova anamva mawu a Aisiraeli ndipo anapereka Akananiwo mʼmanja mwawo. Aisiraeli anawononga Akananiwo limodzi ndi mizinda yawo. Nʼchifukwa chake malowo anawatchula kuti Horima.*+
4 Pamene Aisiraeliwo ankapitiriza ulendo wawo kuchokera kuphiri la Hora+ kudzera njira yopita ku Nyanja Yofiira, pofuna kulambalala dziko la Edomu,+ anthuwo anatopa ndi ulendowo. 5 Choncho iwo anayamba kudandaula motsutsana ndi Mulungu komanso Mose+ kuti: “Nʼchifukwa chiyani munatitulutsa mʼdziko la Iguputo kuti tidzafere mʼchipululu muno? Kuno kulibe chakudya komanso madzi,+ ndipo chakudya chonyansachi chafika potikola.”+ 6 Ndiyeno Yehova anatumiza njoka zapoizoni* pakati pawo, ndipo zinayamba kuwaluma moti Aisiraeli ambiri anafa.+
7 Choncho anthuwo anapita kwa Mose nʼkumuuza kuti: “Tachimwa ife chifukwa cholankhula modandaula potsutsana ndi Yehova ndiponso inuyo.+ Tipepesereni kwa Yehova kuti atichotsere njokazi.” Zitatero Mose anawapepesera kwa Mulungu.+ 8 Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti: “Upange chifanizo cha njoka yapoizoni* ndipo uchiike pamtengo. Ndiye munthu aliyense akalumidwa, aziyangʼana chifanizocho kuti akhalebe ndi moyo.” 9 Nthawi yomweyo Mose anapanga njoka yakopa+ nʼkuiika pamtengo.+ Ndiye munthu akalumidwa ndi njoka nʼkuyangʼana njoka yakopayo, ankakhalabe ndi moyo.+
10 Pambuyo pake Aisiraeli anasamuka nʼkukamanga msasa ku Oboti.+ 11 Kenako anasamuka ku Oboti nʼkukamanga msasa ku Iye-abarimu,+ mʼchipululu choyangʼanizana ndi dziko la Mowabu, chakumʼmawa. 12 Atachoka kumeneko anakamanga msasa mʼchigwa cha Zeredi.*+ 13 Atasamuka kumeneko anakamanga msasa mʼdera la chigwa cha Arinoni, mʼchipululu chochokera kumalire a dziko la Aamori. Chigwa cha Arinoni+ chinali malire pakati pa dziko la Mowabu ndi la Aamori. 14 Nʼchifukwa chake buku la Nkhondo za Yehova limanena za “Vahebi ku Sufa ndi zigwa za Arinoni.* 15 Mitsinje ya mʼzigwazo* imakafika ku Ari ndipo imayenda mʼmalire a dziko la Mowabu.”
16 Atachoka kumeneko anapita ku Beere. Kumeneku ndi kumene kunali chitsime chimene Yehova anauza Mose kuti: “Sonkhanitsa anthuwo kuti ndiwapatse madzi.”
17 Pa nthawi imeneyo Aisiraeli anaimba nyimbo yakuti:
“Tulutsa madzi, chitsime iwe! Vomerezani* nyimboyi!
18 Chitsimechi chinakumbidwa ndi akalonga, chinafukulidwa ndi anthu olemekezeka,
Anachifukula ndi ndodo ya mtsogoleri wa asilikali komanso ndodo zawo.”
Kenako anachoka kuchipululuko nʼkupita ku Matana. 19 Atachoka ku Matana anapita ku Nahaliyeli ndipo atachoka ku Nahaliyeli anapita ku Bamoti.+ 20 Atachoka ku Bamoti anapita kuchigwa chimene chili mʼdziko la Mowabu,+ pafupi ndi chitunda cha Pisiga+ chimene chinayangʼanizana ndi dera la Yesimoni.*+
21 Tsopano Aisiraeli anatuma anthu kuti apite kwa Sihoni mfumu ya Aamori kukanena kuti:+ 22 “Tiloleni tidutse mʼdziko lanu. Sitikhotera mʼmunda uliwonse kapena mʼmunda wa mpesa. Sitimwa madzi pachitsime chilichonse. Tizingoyenda mu Msewu wa Mfumu mpaka titadutsa mʼdziko lanu.”+ 23 Koma Sihoni sanalole kuti Aisiraeli adutse mʼdziko lake. Mʼmalomwake, iye anasonkhanitsa anthu ake onse nʼkupita kukamenyana ndi Aisiraeli mʼchipululumo. Anakafika ku Yahazi ndipo anayamba kumenyana ndi Aisiraeli.+ 24 Koma Aisiraeli anapha anthuwo ndi lupanga+ nʼkuwalanda dziko lawo,+ kuyambira kuchigwa cha Arinoni+ mpaka kuchigwa cha Yaboki,+ pafupi ndi Aamoni, chifukwa Yazeri+ anachita malire ndi Aamoni.+
25 Choncho Aisiraeli analanda mizinda yonseyi nʼkuyamba kukhala mʼmizinda yonse ya Aamori+ ku Hesiboni ndi mʼmidzi yake yonse yozungulira. 26 Anayamba kukhala kumeneko chifukwa Hesiboni unali mzinda wa Sihoni, mfumu ya Aamori, amene anamenyana ndi mfumu ya Mowabu nʼkulanda dziko lake lonse mpaka kukafika kuchigwa cha Arinoni. 27 Nʼchifukwa chake pali ndakatulo yonyoza yakuti:
“Bwerani ku Hesiboni.
Mzinda wa Sihoni umangidwe nʼkukhala wolimba.
28 Chifukwa moto unatuluka ku Hesiboni, lawi lamoto linatuluka mʼtauni ya Sihoni.
Wawotcha Ari mzinda wa ku Mowabu, wawotcha olamulira amʼmalo okwezeka a ku Arinoni.
29 Tsoka iwe Mowabu! Mudzawonongedwa, inu anthu a Kemosi!+
Iye adzapangitsa ana ake aamuna kukhala othawa kwawo, ndipo adzasandutsa ana ake aakazi kukhala akapolo a Sihoni, mfumu ya Aamori.
30 Tiyeni tiwalase.
Hesiboni adzawonongedwa mpaka ku Diboni.+
Tiyeni timusandutse bwinja mpaka ku Nofa,
Moto udzafalikira mpaka ku Medeba.”+
31 Choncho Aisiraeli anayamba kukhala mʼdziko la Aamori. 32 Kenako Mose anatumiza anthu ena kuti akazonde mzinda wa Yazeri.+ Atatero, Aisiraeliwo analanda midzi yozungulira mzindawo, nʼkuthamangitsa Aamori amene anali kumeneko. 33 Pambuyo pake, anatembenuka nʼkulowera Njira ya ku Basana. Ndiyeno Ogi+ mfumu ya ku Basana anabwera limodzi ndi anthu ake onse kudzamenyana nawo ku Edirei.+ 34 Yehova anauza Mose kuti: “Usamuope ameneyu,+ chifukwa ndipereka iyeyo pamodzi ndi anthu ake onse komanso dziko lake mʼmanja mwako+ ndipo umuchitire zimene unachitira Sihoni mfumu ya Aamori, amene ankakhala ku Hesiboni.”+ 35 Choncho Aisiraeliwo anapha iyeyo, ana ake ndi anthu ake onse, moti palibe ndi mmodzi yemwe amene anapulumuka,+ ndipo analanda dziko lake.+
22 Kenako Aisiraeli ananyamuka nʼkukamanga msasa mʼchipululu cha Mowabu, moyangʼanizana ndi Yeriko patsidya pa mtsinje wa Yorodano.+ 2 Tsopano Balaki+ mwana wa Zipori, anaona zonse zimene Aisiraeli anachitira Aamori, 3 ndipo Amowabu anachita mantha kwambiri ndi anthuwo chifukwa anali ambiri. Iwo anagwidwa mantha aakulu chifukwa cha Aisiraeliwo.+ 4 Choncho Amowabuwo anauza akuluakulu a ku Midiyani+ kuti: “Chigulu cha anthuchi chidzadya malo athu onse ngati mmene ngʼombe imadyera msipu kubusa.”
Pa nthawi imeneyo, Balaki mwana wa Zipori ndi amene anali mfumu ya Mowabu. 5 Iye anatumiza anthu kwa Balamu, mwana wa Beori, ku Petori+ pafupi ndi Mtsinje* wamʼdziko lawo. Anawatuma kuti akamuitane kuti: “Taonani! Anthu amene achokera ku Iguputo aja afika kuno. Iwo adzaza dziko lonse lapansi+ kumene munthu angayangʼane, ndipo akukhala pafupi penipeni ndi dziko langa. 6 Tsopano tabwerani chonde, mudzatemberere anthuwa+ chifukwa ndi amphamvu kuposa ineyo. Mwina ndingawagonjetse nʼkuwathamangitsa mʼdziko lino, chifukwa ndikudziwa kuti munthu amene inu mwamudalitsa, amakhaladi wodalitsika, ndipo munthu amene mwamutemberera, amakhaladi wotembereredwa.”
7 Choncho akuluakulu a ku Mowabu ndi a ku Midiyani anapita kwa Balamu+ atatenga ndalama zoti akamulipire kuti awawombezere maula, komanso anamuuza zimene Balaki ananena. 8 Balamu atamva mawuwo anawauza kuti: “Mugone konkuno, ndiyeno ndikuyankhani mogwirizana ndi zimene Yehova angandiuze.” Choncho akalonga a ku Mowabuwo anagonadi kwa Balamu.
9 Kenako Mulungu anafika kwa Balamu nʼkumufunsa kuti:+ “Kodi anthu uli nawowa ndi ndani?” 10 Balamu anayankha Mulungu woonayo kuti: “Balaki mwana wa Zipori, mfumu ya Mowabu ndi amene watumiza anthuwa kuti adzandiuze kuti, 11 ‘Taonani! Anthu amene achokera ku Iguputo aja adzaza dziko lonse lapansi kumene munthu angayangʼane. Tsopano bwerani, mudzatemberere anthuwa.+ Mwina ndingathe kumenyana nawo nʼkuwathamangitsa.’” 12 Koma Mulungu anauza Balamu kuti: “Usapite nawo, ndipo anthuwo usawatemberere chifukwa ndi odalitsidwa.”+
13 Balamu anadzuka mʼmamawa nʼkuuza akalonga a Balakiwo kuti: “Pitani kudziko lanu, chifukwa Yehova wakana kuti ndipite nanu.” 14 Choncho akalonga a ku Mowabuwo ananyamuka nʼkubwerera kwa Balaki, ndipo anakamuuza kuti: “Balamu wakana kubwera nafe.”
15 Koma Balaki anatumizanso akalonga ena, ochuluka komanso olemekezeka kuposa oyamba aja. 16 Iwo anapita kwa Balamu nʼkukamuuza kuti: “Balaki mwana wa Zipori wanena kuti, ‘Musalole kuti china chilichonse chikulepheretseni kubwera kwa ine, 17 chifukwa ndidzakupatsani mphoto yaikulu, ndipo ndidzachita chilichonse chimene mungandiuze. Chonde tabwerani mudzatemberere anthuwa.’” 18 Koma Balamu anayankha atumiki a Balakiwo kuti: “Ngakhale Balaki atandipatsa nyumba yake yodzaza siliva ndi golide, sindingachite chilichonse chosemphana ndi zimene Yehova Mulungu wanga angandilamule, kaya chachingʼono kapena chachikulu.+ 19 Bwanji inunso mugone konkuno usiku walero kuti ndimve zinanso zimene Yehova andiuze.”+
20 Usikuwo Mulungu anafika kwa Balamu nʼkumuuza kuti: “Ngati anthuwa abwera kudzakuitana, pita nawo limodzi. Koma ukalankhule mawu okhawo amene ndikakuuze.”+ 21 Choncho Balamu anadzuka mʼmamawa nʼkumanga chishalo pabulu wake,* ndipo anapita limodzi ndi akalonga a ku Mowabu aja.+
22 Koma Mulungu ataona kuti Balamu akupita, anapsa mtima ndipo mngelo wa Yehova anaima pamsewu kuti amutchingire njira. Balamuyo anali atakwera bulu wake, ndipo anali ndi anyamata ake awiri. 23 Ndiyeno buluyo ataona mngelo wa Yehova ataima pamsewu lupanga lake lili mʼmanja, anayesa kuchoka mumsewu nʼkupatukira kutchire. Koma Balamu anayamba kumʼkwapula kuti abwerere mumsewu. 24 Kenako mngelo wa Yehovayo anakaima panjira yopanikiza imene inali pakati pa minda iwiri ya mpesa ndipo njirayo inali ndi khoma lamiyala uku ndi uku. 25 Buluyo ataonanso mngelo wa Yehova uja, anayamba kudzikanikizira kukhoma, moti anakanikiziranso phazi la Balamu kukhomako. Ndipo Balamu anayamba kumʼkwapulanso buluyo.
26 Tsopano mngelo wa Yehova anasunthiranso patsogolo nʼkukaima pamalo ena opanikiza, pomwe panalibiretu mpata woti nʼkudutsira kudzanja lamanja kapena lamanzere. 27 Buluyo ataonanso mngelo wa Yehova uja, anangokhala pansi, Balamu ali pamsana pake. Choncho Balamu anapsa mtima koopsa, ndipo anapitiriza kumukwapula ndi ndodo yake. 28 Potsirizira pake, Yehova anachititsa kuti buluyo alankhule,*+ ndipo anafunsa Balamu kuti: “Kodi ndakulakwirani chiyani kuti mundikwapule katatu konseka?”+ 29 Balamu anayankha buluyo kuti: “Chifukwa wandipusitsa kwambiri. Moti ndikanakhala ndi lupanga mʼdzanja langa, bwenzi pano nʼtakupha!” 30 Buluyo anafunsanso Balamu kuti: “Kodi si ine bulu wanu amene mwakhala mukukwera moyo wanu wonse mpaka lero? Kodi ndinayamba ndachitapo zimenezi kwa inu?” Iye anayankha kuti: “Ayi!” 31 Kenako Yehova anatsegula maso a Balamu,+ ndipo anaona mngelo wa Yehova ataima panjirapo, lupanga lili mʼmanja. Nthawi yomweyo, Balamu anagwada nʼkuwerama mpaka nkhope yake pansi.
32 Ndiyeno mngelo wa Yehova uja anamʼfunsa kuti: “Nʼchifukwa chiyani wakhala ukukwapula bulu wako maulendo atatu onsewa? Inetu ndabwera kudzakutchingira njira, chifukwa ukupita kukachita zinthu zotsutsana ndi zimene ine ndikufuna.+ 33 Buluyu anandiona ndipo anayesa kundipatukira maulendo atatu onsewa.+ Akanapanda kundipatukira, bwenzi pano nʼtakupha. Koma buluyu nʼkanamusiya kuti akhale ndi moyo.” 34 Balamu anauza mngelo wa Yehovayo kuti: “Ndachimwa, sindinadziwe kuti inuyo munaima pamsewu kudzakumana nane. Koma ngati sizinakusangalatseni, ndikhoza kubwerera.” 35 Koma mngelo wa Yehovayo anauza Balamu kuti: “Pita nawo limodzi anthuwa, koma ukanene zokhazo zimene ndikuuze.” Choncho Balamu anapitiriza ulendo wake limodzi ndi akalonga a Balakiwo.
36 Balaki atamva kuti Balamu wafika, nthawi yomweyo ananyamuka kukamulandira kumzinda wa Mowabu. Mzindawu uli mʼmbali mwa mtsinje wa Arinoni, umene uli mʼmalire a dzikolo. 37 Ndiyeno Balaki anafunsa Balamu kuti: “Kodi sindinatumize anthu kuti adzakuitaneni? Nanga nʼchifukwa chiyani simunabwere? Kodi mukuganiza kuti ineyo sindingathe kukupatsani mphoto yaikulu?”+ 38 Balamu anayankha Balaki kuti: “Si ine ndabwerane! Koma kodi ndikuloledwa kunena chilichonse? Inetu ndilankhula mawu okhawo amene Mulungu angandiuze.”*+
39 Choncho Balamu anatengana ndi Balaki, nʼkupita ku Kiriyati-huzoti. 40 Kumeneko Balaki anapereka nsembe zanyama ya ngʼombe ndi nkhosa, nʼkutumiza ina kwa Balamu ndi akalonga amene anali nawo limodzi. 41 Mʼmawa kutacha, Balaki anakatenga Balamu nʼkupita naye ku Bamoti-baala. Anapita naye kumeneko kuti akathe kuliona bwino gulu lonse la Aisiraeli.+
23 Kenako Balamu anauza Balaki kuti: “Mumange maguwa ansembe okwanira 7+ pamalo ano. Mukatero mundikonzere ngʼombe zamphongo 7 ndi nkhosa zamphongo 7.” 2 Nthawi yomweyo Balaki anachita zimene Balamu anamuuza. Kenako Balaki ndi Balamu anapereka nsembe. Anapereka ngʼombe yamphongo ndi nkhosa yamphongo paguwa lililonse.+ 3 Ndiyeno Balamu anauza Balaki kuti: “Mukhale pompano pafupi ndi nsembe yanu yopsereza ndipo ine ndichoka. Mwina Yehova alankhula nane ndipo zimene andiuzezo ndikuuzani.” Choncho Balamu anapita pamwamba pa phiri.
4 Kenako Mulungu anakumana ndi Balamu+ ndipo iye anauza Mulunguyo kuti: “Ndamanga maguwa ansembe 7 mʼmizere, ndipo ndapereka nsembe ngʼombe yamphongo ndi nkhosa yamphongo paguwa lililonse.” 5 Yehova anauza Balamu+ zoti akanene.* Kenako anamuuza kuti: “Bwerera kwa Balaki, ukamuuze mawu amenewa.” 6 Iye anabwerera kwa Balaki ndipo anapeza kuti Balakiyo limodzi ndi akalonga onse a ku Mowabu aima pafupi ndi nsembe yake yopsereza. 7 Kenako Balamu ananena ndakatulo yakuti:+
“Balaki mfumu ya Mowabu wandibweretsa kuno kuchokera ku Aramu,+
Kuchokera kumapiri akumʼmawa kuti:
‘Bwera, udzanditembererere Yakobo.
Bwera, udzaitanire tsoka pa Isiraeli.’+
8 Ndingathe bwanji kutemberera anthu amene Mulungu sanawatemberere?
Ndipo ndingathe bwanji kuitanira tsoka anthu amene Yehova sanawaitanire tsoka?+
9 Ndikutha kuwaona kuchokera pamwamba pa matanthwe pano,
Ndipo ndikuwaona kuchokera pamwamba pa mapiri pano.
10 Ndani angathe kuwerenga mtundu wa Yakobo, womwe ndi wochuluka ngati fumbi+
Kapena kuwerenga gawo limodzi mwa magawo 4 a Isiraeli?
Ndisiyeni ndife imfa ya munthu wolungama,
Ndipo mapeto anga akhale ngati awo.”
11 Kenako Balaki anauza Balamu kuti: “Nʼchifukwa chiyani mwandichitira zimenezi? Ndakubweretsani kuno kuti mudzatemberere adani anga, koma inu mwawadalitsa.”+ 12 Koma iye anamuyankha kuti: “Kodi sindikuyenera kulankhula zimene Yehova wandiuza?”*+
13 Balaki anauza Balamu kuti: “Tiyeni tipite kumalo ena kumene mungathe kuwaona anthuwo. Simukaona onse, koma mukangoona ochepa. Mukatemberere amenewo.”+ 14 Choncho anamutengera ku Zofimu, pamwamba pa phiri la Pisiga.+ Kumeneko anamanga maguwa ansembe 7, nʼkupereka nsembe ngʼombe yamphongo ndi nkhosa yamphongo paguwa lililonse.+ 15 Ndiyeno Balamu anauza Balaki kuti: “Mukhale pano, pafupi ndi nsembe yanu yopserezayi, koma ine ndikukalankhula ndi Mulungu uko.” 16 Kumeneko Yehova analankhuladi ndi Balamu nʼkumuuza zoti akanene kuti:*+ “Bwerera kwa Balaki ndipo ukamuuze zimene ndakuuza.” 17 Choncho Balamu anabwerera kwa Balaki, ndipo anamupeza akudikirira pafupi ndi nsembe yake yopsereza, akalonga a ku Mowabu ali naye limodzi. Ndiyeno Balaki anafunsa Balamu kuti: “Kodi Yehova wanena chiyani?” 18 Kenako Balamu anayambanso kulankhula mwa ndakatulo kuti:+
“Nyamuka, Balaki iwe, tamvera.
Ndimvetsere, iwe mwana wa Zipori.
19 Mulungu sali ngati munthu amene amanena mabodza,+
Akanena kanthu, kodi angalephere kuchita?
Akalankhula, kodi angalephere kukwaniritsa?+
21 Iye sangalole kuti mphamvu zilizonse zamatsenga zivulaze Yakobo,
Ndipo sangalole kuti Isiraeli akumane ndi vuto lililonse.
Mulungu wake Yehova ali naye,+
Ndipo amamutamanda mofuula monga mfumu yawo.
22 Mulungu akuwatulutsa ku Iguputo.+
Kwa iwo, Iye ali ngati nyanga za ngʼombe yamʼtchire yamphongo.*+
Panopa anthu anganene zokhudza Yakobo kapena kuti Isiraeli kuti:
‘Taonani zimene Mulungu wachita!’
24 Uwu ndi mtundu wa anthu umene udzadzuka ngati mkango,
Udzanyamuka ngati mkango.+
Sudzagona pansi mpaka utadya nyama
Ndi kumwa magazi a nyama zophedwazo.”
25 Atatero Balaki anauza Balamu kuti: “Ngati simungathe kuwatemberera ngakhale pangʼono, ndiye musawadalitsenso.” 26 Balamu anayankha Balaki kuti: “Kodi sindinakuuzeni kuti, ‘Ndichita zonse zimene Yehova wanenaʼ?”+
27 Balaki anauza Balamu kuti: “Chonde tabwerani. Tiyeni tipite kumalo enanso. Mwina kumeneko Mulungu woona angalole kuti mutemberere anthuwa.”+ 28 Choncho Balaki anatenga Balamu nʼkupita naye pamwamba pa phiri la Peori, limene linayangʼanizana ndi Yesimoni.*+ 29 Kenako Balamu anauza Balaki kuti: “Mumange maguwa ansembe 7 pamalo ano ndipo mundikonzere ngʼombe zamphongo 7 ndi nkhosa zamphongo 7.”+ 30 Choncho Balaki anachita zimene Balamu ananena ndipo anapereka nsembe ngʼombe yamphongo ndi nkhosa yamphongo paguwa lililonse.
24 Balamu ataona kuti Yehova akufuna* kudalitsa Aisiraeli, sanapitenso kukafunafuna njira yoti awalodzere,+ mʼmalomwake anayangʼana kuchipululu. 2 Balamu atakweza maso ake nʼkuona Aisiraeli ali mʼmisasa mogwirizana ndi mafuko awo,+ mzimu wa Mulungu unafika pa iye.+ 3 Kenako analankhula mwa ndakatulo kuti:+
“Mawu a Balamu mwana wa Beori,
Mawu a mwamuna amene maso ake atseguka,
4 Mawu a munthu amene wamva mawu a Mulungu,
Amene waona masomphenya a Wamphamvuyonse,
Amene wagwada pansi, maso ake ali otsegula. Mawu ake akuti:+
5 Akongolerenji matenti ako, iwe Yakobo,
Komanso malo ako okhala, iwe Isiraeli!+
6 Andanda kukafika kutali ngati zigwa,*+
Ngati minda mʼmphepete mwa mtsinje.
Ngati mitengo ya aloye imene Yehova anadzala,
Ngati mikungudza mʼmbali mwa madzi.
7 Madzi odzaza mitsuko yake iwiri akutayikirabe pansi,
8 Mulungu akumutulutsa mu Iguputo.
Iye ali ngati nyanga za ngʼombe yamʼtchire yamphongo.
Adzawononga anthu a mitundu ina, amene akumupondereza,+
Adzakungudza* mafupa awo, ndipo adzawaswa ndi mivi yake.
9 Iye wagwada pansi, wagona pansi ngati mkango,
Ngati mkango, ndani angayese kumʼdzutsa?
Amene akudalitsa iwe adzadalitsidwa,
Ndipo amene akukutemberera, adzatembereredwa.”+
10 Kenako Balaki anapsera mtima Balamu. Ndiyeno Balaki anawomba mʼmanja mokwiya nʼkuuza Balamu kuti: “Ndinakuitana kuti udzatemberere adani anga,+ koma iwe wawadalitsa kwambiri maulendo atatu onsewa. 11 Nyamuka pompano uzipita kwanu. Ine ndimafuna ndikupatse mphoto,+ koma taona! Yehova wakulepheretsa kulandira mphoto.”
12 Balamu anayankha Balaki kuti: “Kodi anthu amene munawatuma aja sindinawauze kuti, 13 ‘Ngakhale Balaki atandipatsa nyumba yake yodzaza siliva ndi golide, sindingachite chilichonse chimene ndikufuna,* kaya chabwino kapena choipa, chosemphana ndi zimene Yehova walamula? Kodi sindinanene kuti ndikalankhula zokhazo zimene Yehova akandiuzeʼ?+ 14 Tsopano ndikupita kwa anthu a mtundu wanga. Koma tabwerani kuti ndikuuzeni zimene anthuwa adzachite kwa anthu anu mʼtsogolo.” 15 Kenako analankhula mwa ndakatulo kuti:+
“Mawu a Balamu mwana wa Beori,
Mawu a mwamuna amene maso ake ndi otsegula,+
16 Mawu a munthu amene wamva mawu a Mulungu,
Amene akudziwa Wamʼmwambamwamba,
Anaona masomphenya a Wamphamvuyonse,
Atagwada pansi, maso ake ali otsegula. Mawu ake akuti:
17 Ndidzamuona, koma osati panopa;
Ndidzamupenya, koma osati posachedwa.
Ndipo iye adzaphwanyadi chipumi cha Mowabu+
Ndi mitu ya asilikali onse ankhanza.
18 Edomu adzalandidwa,+
Ndithu Seiri+ adzalandidwa ndi adani ake,+
Pamene Isiraeli akuonetsa kulimba mtima kwake.
19 Wina adzatuluka mwa Yakobo kukagonjetsa,+
Ndipo adzawononga aliyense amene wapulumuka mumzindamo.”
20 Balamu ataona Amaleki, anapitiriza mawu ake a ndakatulo kuti:
21 Ataona Akeni+ anapitiriza kulankhula mwa ndakatulo kuti:
“Mumakhala motetezeka, malo anu okhala ali pathanthwe.
22 Koma Kayini* adzawotchedwa ndi moto.
Kodi padzatenga nthawi yayitali bwanji Asuri asanakugwire nʼkupita nawe kudziko lina?”
23 Anapitiriza kulankhula mwa ndakatulo kuti:
“Mayo ine! Ndani adzapulumuke Mulungu akadzachita zimenezi?
Koma iyenso adzawonongedwa kotheratu.”
25 Kenako Balamu+ ananyamuka nʼkubwerera kwawo. Nayenso Balaki anapita kwawo.
25 Pa nthawi imene Aisiraeli ankakhala ku Sitimu,+ anayamba kuchita chiwerewere ndi akazi a ku Mowabu.+ 2 Akaziwo anaitana Aisiraeliwo kuti azikapereka nsembe kwa milungu yawo+ ndipo Aisiraeliwo anayamba kudya nsembezo komanso kugwadira milungu ya Amowabu.+ 3 Choncho Aisiraeli anayamba kulambira nawo Baala wa ku Peori,+ ndipo Yehova anakwiya kwambiri ndi Aisiraeliwo. 4 Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti: “Gwira onse amene akutsogolera anthuwo, ndipo uwaphe nʼkuwapachika pamtengo pamaso pa Yehova dzuwa likuswa mtengo. Uchite zimenezo kuti mkwiyo wa Yehova umene wayakira Aisiraeli uchoke.” 5 Choncho Mose anauza oweruza a mu Isiraeli kuti:+ “Aliyense wa inu aphe anthu ake amene akulambira nawo Baala wa ku Peori.”+
6 Koma mwadzidzidzi anthuwo anangoona mwamuna wina wa Chiisiraeli akubwera ndi mkazi wa Chimidiyani.+ Anabwera naye kufupi ndi abale ake, pamaso pa Mose ndi gulu lonse la Aisiraeli. Pa nthawiyi nʼkuti Aisiraeliwo akulira pakhomo la chihema chokumanako. 7 Pinihasi+ mwana wa Eleazara, mdzukulu wa wansembe Aroni, ataona zimenezi nthawi yomweyo ananyamuka pakati pa gululo nʼkutenga mkondo* mʼdzanja lake. 8 Iye anathamangira mwamuna wa Chiisiraeli uja mpaka kukalowa mutenti yake ndipo anabaya onse awiriwo ndi mkondowo. Anabaya mwamuna wa Chiisiraeli uja limodzi ndi mkaziyo, mpaka mkondowo unakadutsa kumaliseche kwa mkaziyo. Atatero mliriwo unaleka pakati pa Aisiraeli.+ 9 Amene anafa ndi mliriwo analipo 24,000.+
10 Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti: 11 “Pinihasi+ mwana wa Eleazara, mdzukulu wa wansembe Aroni, wabweza mkwiyo wanga pa Aisiraeli, chifukwa sanalekerere ngakhale pangʼono kuti anthu azipikisana nane pakati pawo.+ Choncho sindinawononge Aisiraeliwa, ngakhale kuti ndimafuna kuti anthu azikhala odzipereka kwa ine ndekha.+ 12 Pa chifukwa chimenechi, umuuze Pinihasi kuti, ‘Ndikupangana naye pangano la mtendere. 13 Limeneli likhala pangano la unsembe kwa iye ndi mbadwa zake mpaka kalekale,+ chifukwa sanalekerere zoti anthu azipikisana ndi Mulungu wake+ ndiponso anaphimba machimo a Aisiraeli.’”
14 Dzina la mwamuna wa Chiisiraeli, amene anaphedwa limodzi ndi mkazi wa Chimidiyani uja linali Zimiri mwana wa Salu, ndipo anali mtsogoleri wa nyumba ya makolo a fuko la Simiyoni. 15 Dzina la mkazi wa Chimidiyani amene anaphedwayo linali Kozibi, mwana wa Zuri.+ Zuri anali mtsogoleri wa fuko la nyumba ina ya makolo ku Midiyani.+
16 Pambuyo pake Yehova anauza Mose kuti: 17 “Akhaulitseni Amidiyani ndipo muwaphe,+ 18 chifukwa akubweretserani tsoka mochenjera pokukopani kuti muchimwe ku Peori.+ Muwaphe ndithu, chifukwanso cha zochita za mchemwali wawo Kozibi, mwana wa mtsogoleri wa ku Midiyani, amene anaphedwa+ pa tsiku limene mliri unakugwerani chifukwa cha zimene zinachitika ku Peori.”+
26 Mliri uja utatha,+ Yehova anauza Mose ndi Eleazara mwana wa wansembe Aroni kuti: 2 “Muwerenge amuna onse oyenera kupita kunkhondo pakati pa gulu lonse la Aisiraeli. Muwerenge kuyambira azaka 20 kupita mʼtsogolo, potengera nyumba za makolo awo.”+ 3 Choncho Mose ndi wansembe Eleazara+ analankhula ndi Aisiraeliwo mʼchipululu cha Mowabu,+ pafupi ndi mtsinje wa Yorodano, kufupi ndi Yeriko kuti:+ 4 “Muwerenge Aisiraeli onse kuyambira azaka 20 kupita mʼtsogolo, mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose.”+
Ana a Isiraeli amene anatuluka mʼdziko la Iguputo anali awa: 5 Rubeni+ anali mwana woyamba kubadwa wa Isiraeli. Ana aamuna a Rubeni+ anali awa: Hanoki amene anali kholo la banja la Ahanoki, Palu amene anali kholo la banja la Apalu, 6 Hezironi amene anali kholo la banja la Ahezironi ndi Karami amene anali kholo la banja la Akarami. 7 Amenewa anali mabanja a anthu a fuko la Rubeni ndipo amuna onse amene anawerengedwa analipo 43,730.+
8 Mwana wamwamuna wa Palu anali Eliyabu. 9 Ana aamuna a Eliyabu anali Nemueli, Datani ndi Abiramu. Awiriwa, Datani ndi Abiramu, ndi amene anasankhidwa pa gululo ndipo anagwirizana ndi gulu la Kora+ pokangana ndi Mose+ komanso Aroni pamene ankatsutsana ndi Yehova.+
10 Zitatero, nthaka inangʼambika* nʼkuwameza. Koma Kora anafa pamene moto unapsereza amuna 250.+ Ndipo iwo anakhala chitsanzo chotichenjeza.+ 11 Koma ana a Kora sanafe.+
12 Ana aamuna a Simiyoni+ potengera mabanja awo anali awa: Nemueli amene anali kholo la banja la Anemueli, Yamini amene anali kholo la banja la Ayamini, Yakini amene anali kholo la banja la Ayakini, 13 Zera amene anali kholo la banja la Azera ndi Shauli amene anali kholo la banja la Ashauli. 14 Mabanja a anthu a fuko la Simiyoni anali amenewa. Amuna onse pamodzi analipo 22,200.+
15 Ana aamuna a Gadi+ potengera mabanja awo anali awa: Zefoni amene anali kholo la banja la Azefoni, Hagi amene anali kholo la banja la Ahagi, Suni amene anali kholo la banja la Asuni, 16 Ozini amene anali kholo la banja la Aozini, Eri amene anali kholo la banja la Aeri, 17 Arodi amene anali kholo la banja la Aarodi ndi Areli amene anali kholo la banja la Aareli. 18 Amenewa anali mabanja a ana a Gadi. Amuna onse amene anawerengedwa analipo 40,500.+
19 Ana a Yuda+ anali Ere ndi Onani.+ Koma awiriwa anafera mʼdziko la Kanani.+ 20 Choncho ana aamuna a Yuda mwa mabanja awo anali awa: Shela+ amene anali kholo la banja la Ashela, Perezi+ amene anali kholo la banja la Aperezi ndi Zera+ amene anali kholo la banja la Azera. 21 Ana aamuna a Perezi anali Hezironi+ amene anali kholo la banja la Ahezironi ndi Hamuli+ amene anali kholo la banja la Ahamuli. 22 Amenewa anali mabanja a Yuda. Amuna onse amene anawerengedwa analipo 76,500.+
23 Ana aamuna a Isakara+ potengera mabanja awo anali awa: Tola+ amene anali kholo la banja la Atola, Puva amene anali kholo la banja la Apuna, 24 Yasubi amene anali kholo la banja la Ayasubi ndi Simironi amene anali kholo la banja la Asimironi. 25 Amenewa anali mabanja a Isakara. Amuna onse amene anawerengedwa analipo 64,300.+
26 Ana aamuna a Zebuloni+ anali awa: Seredi amene anali kholo la banja la Aseredi, Eloni amene anali kholo la banja la Aeloni ndi Yahaleeli amene anali kholo la banja la Ayahaleeli. 27 Amenewa anali mabanja a anthu a fuko la Zebuloni. Amuna onse amene anawerengedwa analipo 60,500.+
28 Ana aamuna a Yosefe+ potengera mabanja awo anali Manase ndi Efuraimu.+ 29 Ana aamuna a Manase+ anali Makiri+ amene anali kholo la banja la Amakiri. Makiri anabereka Giliyadi. Giliyadi anali kholo la banja la Agiliyadi.+ 30 Ana aamuna a Giliyadi anali awa: Yezeri amene anali kholo la banja la Ayezeri, Heleki amene anali kholo la banja la Aheleki, 31 Asiriyeli amene anali kholo la banja la Aasiriyeli, Sekemu amene anali kholo la banja la Asekemu, 32 Semida amene anali kholo la banja la Asemida ndi Heferi amene anali kholo la banja la Aheferi. 33 Koma Tselofekadi, mwana wamwamuna wa Heferi, analibe ana aamuna koma aakazi okhaokha.+ Mayina a ana aakazi a Tselofekadi+ anali: Mala, Nowa, Hogila, Milika ndi Tiriza. 34 Amenewa anali mabanja a Manase. Amuna onse amene anawerengedwa analipo 52,700.+
35 Ana aamuna a Efuraimu+ potengera mabanja awo anali awa: Sutela+ amene anali kholo la banja la Asutela, Bekeri amene anali kholo la banja la Abekeri ndi Tahani amene anali kholo la banja la Atahani. 36 Ana aamuna a Sutela anali Erani amene anali kholo la banja la Aerani. 37 Amenewa anali mabanja a ana a Efuraimu. Amuna onse amene anawerengedwa analipo 32,500.+ Awa anali ana aamuna a Yosefe potengera mabanja awo.
38 Ana aamuna a Benjamini+ potengera mabanja awo anali awa: Bela+ amene anali kholo la banja la Abela, Asibeli amene anali kholo la banja la Aasibeli, Ahiramu amene anali kholo la banja la Aahiramu, 39 Sefufamu amene anali kholo la banja la Asefufamu ndi Hufamu amene anali kholo la banja la Ahufamu. 40 Ana aamuna a Bela anali Aridi ndi Namani.+ Aridi anali kholo la banja la Aaridi. Namani anali kholo la banja la Anamani. 41 Amenewa anali ana aamuna a Benjamini potengera mabanja awo. Amuna onse amene anawerengedwa analipo 45,600.+
42 Ana aamuna a Dani+ potengera mabanja awo anali ochokera kwa Suhamu amene anali kholo la banja la Asuhamu. Awa anali mabanja a Dani potengera fuko lawo. 43 Amuna onse amene anawerengedwa mʼmabanja a Asuhamu analipo 64,400.+
44 Ana aamuna a Aseri+ potengera mabanja awo anali awa: Imuna amene anali kholo la banja la Aimuna, Isivi amene anali kholo la banja la Aisivi ndi Beriya amene anali kholo la banja la Aberiya. 45 Ana aamuna a Beriya anali Hiberi amene anali kholo la banja la Ahiberi ndi Malikieli amene anali kholo la banja la Amalikieli. 46 Mwana wamkazi wa Aseri anali Sera. 47 Amenewa anali mabanja a ana aamuna a Aseri. Amuna onse amene anawerengedwa analipo 53,400.+
48 Ana aamuna a Nafitali+ potengera mabanja awo anali awa: Yahazeeli amene anali kholo la banja la Ayahazeeli, Guni amene anali kholo la banja la Aguni, 49 Yezera amene anali kholo la banja la Ayezera ndi Silemu amene anali kholo la banja la Asilemu. 50 Amenewa anali mabanja a Nafitali potengera fuko lawo. Amuna onse amene anawerengedwa analipo 45,400.+
51 Amuna onse amene anawerengedwa pakati pa Aisiraeli ndi amenewa ndipo onse pamodzi analipo 601,730.+
52 Pambuyo pake Yehova anauza Mose kuti: 53 “Anthu amenewa uwagawire dzikoli kuti likhale cholowa chawo, potengera mndandanda wa mayinawo.*+ 54 Amene ali ndi anthu ambiri apatsidwe dziko lalikulu monga cholowa chake, ndipo amene ali ndi anthu ochepa apatsidwe dziko lalingʼono monga cholowa chake.+ Aliyense apatsidwe cholowacho mogwirizana ndi chiwerengero cha anthu ake. 55 Koma dzikolo uligawe pochita maere.+ Onse alandire cholowa chawo potengera mayina a mafuko a makolo awo. 56 Muchite maere kuti mudziwe cholowa cha fuko lililonse, kaya lili ndi anthu ambiri kapena ochepa.”
57 Tsopano awa ndi mayina a amuna amene anawerengedwa pakati pa Alevi+ potengera mabanja awo: Agerisoni, a banja la Gerisoni, Akohati, a banja la Kohati+ ndi Amerari, a banja la Merari. 58 Mabanja a Alevi ndi awa: banja la Alibini,+ banja la Aheburoni,+ banja la Amali,+ banja la Amusi+ ndi banja la Akora.+
Kohati anabereka Amuramu.+ 59 Mkazi wa Amuramu anali Yokebedi,+ mwana wa Levi. Mkazi wa Levi anamuberekera mwana ameneyu ku Iguputo. Yokebedi anaberekera Amuramu ana awa: Aroni, Mose ndi mchemwali wawo Miriamu.+ 60 Kenako Aroni anabereka Nadabu, Abihu, Eleazara ndi Itamara.+ 61 Koma Nadabu ndi Abihu anafa chifukwa chopereka moto wosaloleka pamaso pa Yehova.+
62 Onse amene anawerengedwa pakati pa Alevi analipo 23,000. Amenewa anali amuna onse kuyambira amwezi umodzi kupita mʼtsogolo.+ Iwo sanawerengedwe limodzi ndi Aisiraeli,+ chifukwa sanafunikire kulandira cholowa pakati pa Aisiraeli.+
63 Awa ndi anthu amene Mose ndi wansembe Eleazara anawawerenga pakati pa Aisiraeli. Anawawerengera mʼchipululu cha Mowabu, pafupi ndi mtsinje wa Yorodano, kufupi ndi Yeriko. 64 Koma pakati pa anthu amenewa, panalibe munthu aliyense amene anali mʼgulu la anthu omwe anawerengedwa mʼchipululu cha Sinai, nthawi imene Mose ndi wansembe Aroni anawerenga Aisiraeli.+ 65 Zinakhala choncho chifukwa ponena za iwo, Yehova anati: “Ndithu anthu amenewa adzafera mʼchipululu.”+ Choncho, palibe amene anatsala kupatulapo Kalebe mwana wa Yefune ndi Yoswa mwana wa Nuni.+
27 Kenako ana aakazi a Tselofekadi+ anafika kwa Mose. Tselofekadi anali mwana wa Heferi, Heferi anali mwana wa Giliyadi, Giliyadi anali mwana wa Makiri ndipo Makiri anali mwana wa Manase. Onsewa anali ochokera kumabanja a Manase mwana wa Yosefe. Ana aakazi a Tselofekadi amenewa mayina awo anali Mala, Nowa, Hogila, Milika ndi Tiriza. 2 Iwo anakaimirira pamaso pa Mose, wansembe Eleazara, atsogoleri+ komanso gulu lonse, pakhomo la chihema chokumanako nʼkunena kuti: 3 “Bambo athu anafera mʼchipululu. Koma iwo sanali mʼgulu la anthu amene ankatsatira Kora,+ omwe anasonkhana kuti atsutsane ndi Yehova. Bambo athuwo anafa chifukwa cha tchimo lawo, ndipo analibe mwana aliyense wamwamuna. 4 Kodi dzina la bambo athu lisapezekenso ku banja lawo chifukwa chakuti analibe mwana wamwamuna? Chonde, tipatseni cholowa pakati pa azichimwene a bambo athu.” 5 Choncho Mose anapereka dandaulo lawolo pamaso pa Yehova.+
6 Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti: 7 “Ana aakazi a Tselofekadi akunena zoona. Uwapatsedi malo kuti akhale cholowa chawo pakati pa azichimwene a bambo awo. Cholowa cha bambo awocho chikhale chawo.+ 8 Ndipo uuze Aisiraeli kuti: ‘Ngati mwamuna wamwalira alibe mwana wamwamuna, muzipereka cholowa chake kwa mwana wake wamkazi. 9 Ngati alibe mwana wamkazi, muzipereka cholowa chake kwa azichimwene ake. 10 Ngati alibe azichimwene, muzipereka cholowa chake kwa azichimwene a bambo ake. 11 Ngati bambo ake alibe azichimwene awo, muzipereka cholowa chake kwa wachibale wake wapafupi wa ku banja lawo, ndipo azitenga cholowacho kuti chikhale chake. Chigamulo chimenechi chidzakhala lamulo kwa Aisiraeli, mogwirizana ndi zimene Yehova walamula Mose.’”
12 Kenako Yehova anauza Mose kuti: “Kwera phiri ili la Abarimu,+ ukaone dziko limene ndidzalipereke kwa Aisiraeli.+ 13 Ukaliona dzikolo, iwenso udzaikidwa mʼmanda ngati mmene anachitira ndi makolo ako*+ komanso Aroni mchimwene wako,+ 14 chifukwa pamene gulu lija linakangana nane mʼchipululu cha Zini, inu munapandukira mawu anga ndipo munalephera kundilemekeza pamaso pa gululo pamadzi+ a Meriba+ ku Kadesi,+ mʼchipululu cha Zini.”+
15 Kenako Mose anauza Yehova kuti: 16 “Inu Yehova, Mulungu amene mumapereka moyo kwa anthu onse,* sankhani munthu woti azitsogolera gululi. 17 Musankhe munthu woti akhale mtsogoleri wawo pa zinthu zonse, woti aziwatsogolera pa zochita zawo zonse, kuti gulu la Yehova lisakhale ngati nkhosa zopanda mʼbusa.” 18 Choncho Yehova anauza Mose kuti: “Tenga Yoswa mwana wa Nuni, munthu wolimba mtima,* ndipo uike dzanja lako pa iye.+ 19 Kenako umuimiritse pamaso pa wansembe Eleazara komanso pamaso pa gulu lonse, ndipo umuike kuti akhale mtsogoleri pamaso pawo.+ 20 Umupatseko mphamvu zako,*+ kuti gulu lonse la Aisiraeli lizimumvera.+ 21 Yoswayo aziimirira pamaso pa wansembe Eleazara, ndipo Eleazara azifunsira chigamulo cha Yehova mʼmalo mwa Yoswayo pogwiritsa ntchito maere a Urimu.+ Aliyense azitsatira zimene walamula* kaya ndi Yoswayo, Aisiraeli komanso gulu lonse.”
22 Choncho Mose anachitadi mogwirizana ndi zimene Yehova anamulamula. Anatenga Yoswa nʼkumuimiritsa pamaso pa wansembe Eleazara komanso pamaso pa gulu lonselo. 23 Kenako anaika manja ake pa iye nʼkumuika kukhala mtsogoleri+ mogwirizana ndi zimene Yehova ananena kudzera mwa Mose.+
28 Kenako Yehova anauza Mose kuti: 2 “Lamula Aisiraeli kuti, ‘Muzionetsetsa kuti mukupereka kwa ine nsembe yanga, yomwe ndi chakudya changa. Pa nthawi yake yoikidwiratu muzipereka nsembe zanga zowotcha pamoto, kuti zikhale kafungo kosangalatsa* kwa ine.’+
3 Uwauze kuti, ‘Nsembe yowotcha pamoto imene muzipereka kwa Yehova ndi iyi: tsiku lililonse muzipereka nsembe yopsereza ya ana a nkhosa awiri amphongo, achaka chimodzi komanso opanda chilema.+ 4 Mwana wa nkhosa mmodzi wamphongo muzimupereka nsembe mʼmamawa. Ndipo mwana wa nkhosa wamphongo winayo, muzimupereka nsembe madzulo kuli kachisisira.*+ 5 Muzipereka nsembezi limodzi ndi ufa wosalala wokwana gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa efa,* kuti ikhale nsembe yambewu. Ufawo muziuthira mafuta oyenga bwino kwambiri okwana gawo limodzi mwa magawo 4 a muyezo wa hini.*+ 6 Imeneyi ndi nsembe yopsereza+ ya tsiku ndi tsiku imene ndinakulamulani kuphiri la Sinai. Ndinakulamulani kuti muziipereka kwa Yehova kuti ikhale nsembe yakafungo kosangalatsa,* yowotcha pamoto. 7 Muziipereka pamodzi ndi nsembe yachakumwa chokwana gawo limodzi mwa magawo 4 a muyezo wa hini. Pa mwana wa nkhosa wamphongo aliyense+ muzipereka nsembe yachakumwa. Muzithirira Yehova nsembe yachakumwa choledzeretsa mʼmalo oyera. 8 Mwana wa nkhosa wamphongo winayo muzimupereka nsembe madzulo kuli kachisisira.* Muzimupereka limodzi ndi nsembe yambewu ndiponso yachakumwa, mofanana ndi nsembe ya mʼmamawa ija. Izikhala nsembe yowotcha pamoto yakafungo kosangalatsa* kwa Yehova.+
9 Koma pa tsiku la Sabata,+ muzipereka nsembe ana a nkhosa awiri amphongo opanda chilema. Muziwapereka pamodzi ndi ufa wosalala kuti ikhale nsembe yambewu. Ufawo muziuthira mafuta, ndipo uzikhala wokwana magawo awiri mwa magawo 10 a muyezo wa efa. Muziperekanso nsembe yake yachakumwa. 10 Imeneyi ndi nsembe yopsereza ya tsiku la Sabata, ndipo muziipereka nthawi zonse limodzi ndi nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku komanso nsembe yake yachakumwa.+
11 Kumayambiriro kwa mwezi uliwonse,* muzipereka nsembe yopsereza kwa Yehova. Muzipereka ngʼombe ziwiri zazingʼono zamphongo, nkhosa imodzi yamphongo ndi ana a nkhosa 7 amphongo opanda chilema. Mwana wa nkhosa aliyense azikhala wachaka chimodzi.+ 12 Pa ngʼombe iliyonse yamphongo, muzipereka ufa wosalala wothira mafuta wokwana magawo atatu mwa magawo 10 a muyezo wa efa, kuti ikhale nsembe yake yambewu.+ Nkhosa yamphongo imodziyo muziipereka limodzi ndi nsembe yambewu ya ufa wosalala wothira mafuta, wokwana magawo awiri mwa magawo 10 a muyezo wa efa.+ 13 Ndipo pa mwana wa nkhosa wamphongo aliyense, yemwe ndi nsembe yopsereza yakafungo kosangalatsa,*+ nsembe yowotcha pamoto yoperekedwa kwa Yehova, muziperekanso nsembe yambewu ya ufa wosalala wothira mafuta. Ufawo uzikhala wokwana gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa efa. 14 Pa nyama iliyonse yoperekedwa nsembe, muziperekanso nsembe yachakumwa. Ngʼombe yamphongo muziipereka limodzi ndi vinyo+ wokwana hafu ya muyezo wa hini. Nkhosa yamphongo+ muziipereka limodzi ndi vinyo wokwana gawo limodzi mwa magawo atatu a muyezo wa hini. Ndipo mwana wa nkhosa wamphongo muzimupereka limodzi ndi vinyo wokwana gawo limodzi mwa magawo 4 a muyezo wa hini.+ Zinthu zimenezi muzizipereka monga nsembe yopsereza ya mwezi ndi mwezi ndipo muzizipereka mwezi uliwonse pa chaka. 15 Muziperekanso mbuzi yaingʼono kuti ikhale nsembe yamachimo kwa Yehova, kuwonjezera pa nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku, limodzi ndi nsembe yake yachakumwa.
16 Mʼmwezi woyamba, pa tsiku la 14, pazikhala Pasika wa Yehova.+ 17 Ndiyeno pa tsiku la 15 la mwezi umenewu pazikhala chikondwerero. Kwa masiku 7 muzidya mikate yopanda zofufumitsa.+ 18 Pa tsiku loyamba la chikondwererocho muzichita msonkhano wopatulika. Musamagwire ntchito iliyonse yotopetsa pa tsikuli. 19 Muzipereka nsembe yopsereza kwa Yehova, yomwe ndi nsembe yowotcha pamoto. Muzipereka ngʼombe ziwiri zazingʼono zamphongo, nkhosa imodzi yamphongo ndi ana a nkhosa 7 amphongo. Mwana wa nkhosa aliyense azikhala wachaka chimodzi. Muzionetsetsa kuti nyamazo nʼzopanda chilema.+ 20 Muzipereka nsembe zimenezi limodzi ndi nsembe zake zambewu. Ngʼombe yamphongo iliyonse muziipereka limodzi ndi ufa wosalala wokwana magawo atatu mwa magawo 10 a muyezo wa efa. Nkhosa yamphongoyo muziipereka limodzi ndi ufa wokwana magawo awiri mwa magawo 10 a muyezo wa efa. Ufawo uzikhala wothira mafuta.+ 21 Pa mwana wa nkhosa wamphongo aliyense pa ana a nkhosa 7 amenewo, muziperekanso ufa wokwana gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa efa. 22 Komanso muzipereka mbuzi imodzi monga nsembe yamachimo, kuti ikhale yophimbira machimo anu. 23 Muzipereka nsembe zimenezi, kuwonjezera pa nsembe yopsereza yamʼmamawa ya tsiku ndi tsiku. 24 Muzipereka nsembe zimenezi mofanana tsiku lililonse kwa masiku 7. Muzizipereka monga chakudya, nsembe yowotcha pamoto yakafungo kosangalatsa* kwa Yehova. Muziipereka limodzi ndi nsembe yopsereza ya nthawi zonse komanso nsembe yake yachakumwa. 25 Pa tsiku la 7 muzichita msonkhano wopatulika.+ Musamagwire ntchito iliyonse yotopetsa pa tsikuli.+
26 Ndipo pa tsiku la zipatso zoyamba kucha,+ pamene muzipereka nsembe yambewu zatsopano kwa Yehova,+ paphwando lanu la masabata, muzichita msonkhano wopatulika.+ Musamagwire ntchito iliyonse yotopetsa pa tsikuli.+ 27 Muzipereka nsembe yopsereza yakafungo kosangalatsa* kwa Yehova. Muzipereka ngʼombe ziwiri zazingʼono zamphongo, nkhosa imodzi yamphongo ndi ana a nkhosa 7 amphongo, achaka chimodzi.+ 28 Muziperekanso nsembe yake yambewu ya ufa wosalala wothira mafuta. Ufawo uzikhala wokwana magawo atatu mwa magawo 10 a muyezo wa efa pa ngʼombe yamphongo iliyonse. Pa nkhosa yamphongo imodziyo, muzipereka ufa wokwana magawo awiri mwa magawo 10 a muyezo wa efa. 29 Pa aliyense wa ana a nkhosa amphongo 7 amenewo, muzipereka ufa wokwana gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa efa. 30 Komanso muzipereka mbuzi yaingʼono yophimbira machimo anu.+ 31 Muzipereka zimenezi kuwonjezera pa nsembe yanu yopsereza ya nthawi zonse ndi nsembe yake yambewu. Muzionetsetsa kuti nyamazo nʼzopanda chilema+ ndipo muzipereka limodzi ndi nsembe yake yachakumwa.’”
29 “‘Pa tsiku loyamba la mwezi wa 7, muzichita msonkhano wopatulika. Musamagwire ntchito iliyonse yotopetsa.+ Tsiku limeneli lizikhala tsiku loliza lipenga.+ 2 Pa tsikuli muzipereka nsembe yopsereza yakafungo kosangalatsa* kwa Yehova. Muzipereka ngʼombe yaingʼono yamphongo imodzi, nkhosa imodzi yamphongo ndi ana a nkhosa amphongo 7, ndipo mwana wa nkhosa aliyense azikhala wachaka chimodzi, zonse zizikhala zopanda chilema. 3 Muziperekanso ufa wosalala wothira mafuta monga nsembe zake zambewu. Ufawo uzikhala wokwana magawo atatu mwa magawo 10 a muyezo wa efa pa ngʼombe yamphongoyo, magawo awiri mwa magawo 10 pa nkhosa yamphongoyo 4 ndi gawo limodzi mwa magawo 10 pa aliyense wa ana a nkhosa amphongo 7 amenewo. 5 Muziperekanso mbuzi yaingʼono imodzi yamphongo, monga nsembe yamachimo yophimbira machimo anu. 6 Muzipereka nsembe zimenezi kuwonjezera pa nsembe yopsereza ya mwezi ndi mwezi, limodzi ndi nsembe yake yambewu.+ Muzizipereka kuwonjezeranso pa nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku, limodzi ndi nsembe yake yambewu,+ limodzinso ndi nsembe zachakumwa.+ Muzipereka nsembe zopserezazo mogwirizana ndi dongosolo lake la nthawi zonse, monga nsembe zowotcha pamoto zakafungo kosangalatsa* kwa Yehova.
7 Pa tsiku la 10 la mwezi wa 7 umenewu, muzichita msonkhano wopatulika,+ ndipo muzisonyeza kuti mukudzimvera chisoni chifukwa cha machimo anu.* Musamagwire ntchito iliyonse.+ 8 Pa tsikuli muzipereka nsembe yopsereza yakafungo kosangalatsa* kwa Yehova. Muzipereka ngʼombe yaingʼono yamphongo imodzi, nkhosa yamphongo imodzi ndi ana a nkhosa 7 amphongo, ndipo mwana wa nkhosa aliyense azikhala wachaka chimodzi. Nyama zonsezo zizikhala zopanda chilema.+ 9 Muziperekanso nsembe zake zambewu za ufa wosalala wothira mafuta. Popereka ngʼombe yamphongoyo muziperekanso ufa wokwana magawo atatu mwa magawo 10 a muyezo wa efa. Popereka nkhosa yamphongoyo muziperekanso ufa wokwana magawo awiri mwa magawo 10 a muyezo wa efa. 10 Popereka aliyense mwa ana a nkhosa 7 amphongowo, muziperekanso ufa wokwana gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa efa. 11 Muziperekanso mbuzi yaingʼono imodzi monga nsembe yamachimo. Muziipereka kuwonjezera pa nsembe yamachimo pa tsiku lophimba machimo,+ ndi nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku, limodzi ndi nsembe zake zambewu ndiponso zachakumwa.
12 Pa tsiku la 15 la mwezi wa 7, muzichita msonkhano wopatulika. Musamagwire ntchito iliyonse yotopetsa. Muzichita chikondwerero posonyeza kulemekeza Yehova masiku 7.+ 13 Pa tsiku limeneli muzipereka nsembe yopsereza+ yowotcha pamoto yakafungo kosangalatsa* kwa Yehova. Muzipereka ngʼombe 13 zazingʼono zamphongo, nkhosa zamphongo ziwiri ndi ana a nkhosa 14 amphongo, ndipo mwana wa nkhosa aliyense azikhala wachaka chimodzi, zonse zizikhala zopanda chilema.+ 14 Muziperekanso nsembe zake zambewu za ufa wosalala wothira mafuta. Iliyonse ya ngʼombe 13 zamphongozo muziiperekera ufa wokwana magawo atatu mwa magawo 10 a muyezo wa efa. Iliyonse ya nkhosa zamphongo ziwirizo muziiperekera ufa wokwana magawo awiri mwa magawo 10 a muyezo wa efa. 15 Aliyense wa ana a nkhosa 14 amphongowo, muzimuperekera ufa wokwana gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa efa. 16 Muziperekanso mbuzi yaingʼono imodzi monga nsembe yamachimo, kuwonjezera pa nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku, limodzi ndi nsembe yake yambewu ndiponso nsembe yake yachakumwa.+
17 Pa tsiku lachiwiri, muzipereka ngʼombe 12 zazingʼono zamphongo, nkhosa ziwiri zamphongo, ana a nkhosa 14 amphongo, ndipo mwana wa nkhosa aliyense azikhala wachaka chimodzi, zonse zizikhala zopanda chilema.+ 18 Popereka ngʼombe zamphongo, nkhosa zamphongo ndi ana a nkhosa amphongo, muziperekanso nsembe zake zambewu ndi nsembe zake zachakumwa, mogwirizana ndi kuchuluka kwa nyamazo, potsatira dongosolo la nthawi zonse. 19 Muziperekanso mbuzi yaingʼono imodzi monga nsembe yamachimo. Muziipereka kuwonjezera pa nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku ndi nsembe yake yambewu, limodzi ndi nsembe zake zachakumwa.+
20 Pa tsiku lachitatu, muzipereka ngʼombe 11 zamphongo, nkhosa ziwiri zamphongo ndi ana a nkhosa 14 amphongo, ndipo mwana wa nkhosa aliyense azikhala wachaka chimodzi, zonse zizikhala zopanda chilema.+ 21 Popereka ngʼombe zamphongo, nkhosa zamphongo ndi ana a nkhosa amphongo, muziperekanso nsembe zake zambewu ndi nsembe zake zachakumwa, mogwirizana ndi kuchuluka kwa nyamazo, potsatira dongosolo la nthawi zonse. 22 Muziperekanso mbuzi imodzi monga nsembe yamachimo, kuwonjezera pa nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku, limodzi ndi nsembe yake yambewu, ndiponso nsembe yake yachakumwa.+
23 Pa tsiku la 4, muzipereka ngʼombe 10 zamphongo, nkhosa ziwiri zamphongo, ndi ana a nkhosa 14 amphongo, ndipo mwana wa nkhosa aliyense azikhala wachaka chimodzi, zonse zizikhala zopanda chilema.+ 24 Popereka ngʼombe zamphongo, nkhosa zamphongo ndi ana a nkhosa amphongo, muziperekanso nsembe zake zambewu ndi nsembe zake zachakumwa, mogwirizana ndi kuchuluka kwa nyamazo, potsatira dongosolo la nthawi zonse. 25 Muziperekanso mbuzi yaingʼono imodzi monga nsembe yamachimo, kuwonjezera pa nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku, limodzi ndi nsembe yake yambewu, ndiponso nsembe yake yachakumwa.+
26 Pa tsiku la 5, muzipereka ngʼombe 9 zamphongo, nkhosa ziwiri zamphongo, ndi ana a nkhosa 14 amphongo, ndipo mwana wa nkhosa aliyense azikhala wachaka chimodzi, zonse zizikhala zopanda chilema.+ 27 Popereka ngʼombe zamphongo, nkhosa zamphongo ndi ana a nkhosa amphongo, muziperekanso nsembe zake zambewu ndi nsembe zake zachakumwa, mogwirizana ndi kuchuluka kwa nyamazo, potsatira dongosolo la nthawi zonse. 28 Muziperekanso mbuzi imodzi monga nsembe yamachimo, kuwonjezera pa nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku, limodzi ndi nsembe yake yambewu, ndiponso nsembe yake yachakumwa.+
29 Pa tsiku la 6, muzipereka ngʼombe 8 zamphongo, nkhosa ziwiri zamphongo ndi ana a nkhosa 14 amphongo, ndipo mwana wa nkhosa aliyense azikhala wachaka chimodzi, zonse zizikhala zopanda chilema.+ 30 Popereka ngʼombe zamphongo, nkhosa zamphongo ndi ana a nkhosa amphongo, muziperekanso nsembe zake zambewu ndi nsembe zake zachakumwa, mogwirizana ndi kuchuluka kwa nyamazo, potsatira dongosolo la nthawi zonse. 31 Muziperekanso mbuzi imodzi monga nsembe yamachimo, kuwonjezera pa nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku, limodzi ndi nsembe yake yambewu, ndiponso nsembe yake yachakumwa.+
32 Pa tsiku la 7, muzipereka ngʼombe 7 zamphongo, nkhosa ziwiri zamphongo ndi ana a nkhosa 14 amphongo, ndipo mwana wa nkhosa aliyense azikhala wachaka chimodzi, zonse zizikhala zopanda chilema.+ 33 Popereka ngʼombe zamphongo, nkhosa zamphongo ndi ana a nkhosa amphongo, muziperekanso nsembe zake zambewu ndi nsembe zake zachakumwa, mogwirizana ndi kuchuluka kwa nyamazo, potsatira dongosolo la nthawi zonse la nsembezi. 34 Muziperekanso mbuzi imodzi monga nsembe yamachimo, kuwonjezera pa nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku, limodzi ndi nsembe yake yambewu, ndiponso nsembe yake yachakumwa.+
35 Pa tsiku la 8, muzichita msonkhano wapadera. Musamagwire ntchito iliyonse yotopetsa.+ 36 Pa tsikuli, muzipereka nsembe yopsereza yowotcha pamoto yakafungo kosangalatsa* kwa Yehova. Muzipereka ngʼombe imodzi yamphongo, nkhosa imodzi yamphongo ndi ana a nkhosa 7 amphongo, ndipo mwana wa nkhosa aliyense azikhala wachaka chimodzi, zonse zizikhala zopanda chilema.+ 37 Popereka ngʼombe yamphongo, nkhosa yamphongo ndi ana a nkhosa amphongo, muziperekanso nsembe zake zambewu ndi nsembe zake zachakumwa, mogwirizana ndi kuchuluka kwa nyamazo, potsatira dongosolo la nthawi zonse. 38 Muziperekanso mbuzi imodzi monga nsembe yamachimo, kuwonjezera pa nsembe yopsereza ya tsiku ndi tsiku, limodzi ndi nsembe yake yambewu, ndiponso nsembe yake yachakumwa.+
39 Muzipereka zimenezi kwa Yehova pa zikondwerero zanu,+ kuwonjezera pa nsembe zimene mukupereka chifukwa cha lonjezo limene munapanga,+ nsembe zanu zaufulu+ zimene mumapereka kuti zikhale nsembe zanu zopsereza,+ nsembe zanu zambewu,+ nsembe zanu zachakumwa+ ndi nsembe zanu zamgwirizano.’”+ 40 Mose anauza Aisiraeli zonse zimene Yehova anamulamula.
30 Ndiyeno Mose analankhula ndi atsogoleri+ a mafuko a Isiraeli kuti: “Tamverani zimene Yehova walamula: 2 Munthu akalonjeza+ kwa Yehova kapena akachita lumbiro+ lodzimana, asalephere kukwaniritsa mawu ake.+ Azichita zonse zimene walonjezazo.+
3 Mtsikana amene akukhala mʼnyumba ya bambo ake akalonjeza zinazake kwa Yehova, kapena akachita lumbiro lodzimana, 4 bambo ake nʼkumumva akulonjeza kapena akuchita lumbiro lodzimanalo, koma osamutsutsa, malonjezo ake onsewo akhale momwemo ndipo lumbiro lake lililonse lodzimana likhale momwemo. 5 Koma ngati bambo ake amukaniza atamva zimene walonjeza kapena lumbiro lake lodzimana, malonjezowo akhale opanda ntchito. Yehova adzamukhululukira chifukwa bambo ake anamukaniza.+
6 Koma ngati mtsikanayo wakwatiwa atalumbira kale kapena atalonjeza mosaganiza bwino, 7 ndiyeno mwamuna wake nʼkumva koma osamuletsa pa tsiku limene wamva zimene analonjezazo, malonjezo ake kapena malumbiro akudzimana amene anachitawo azikhala momwemo. 8 Koma mwamuna wake akamukaniza pa tsiku limene wamva zimene analonjezazo, ndiye kuti wafafaniza lonjezo kapena lumbiro limene mkaziyo anachita mosaganiza bwino+ ndipo Yehova adzamukhululukira mkaziyo.
9 Koma mkazi wamasiye kapena amene banja lake linatha akachita lonjezo, lonjezo lililonse limene wachita lizikhala momwemo.
10 Komabe ngati mkazi walonjeza, kapena ngati wachita lumbiro lodzimana, akukhala mʼnyumba ya mwamuna wake, 11 mwamuna wake nʼkumva koma osamutsutsa kapena kumukaniza, malonjezo ake onse, kapena lumbiro lililonse lodzimana limene wachita lizikhala momwemo. 12 Koma mwamuna wake akafafaniza malonjezowo pa tsiku limene wamva zimene mkaziyo analonjeza kapena malumbiro ake odzimana amene anachita, malonjezowo azikhala opanda ntchito.+ Mwamuna wake wawafafaniza ndipo Yehova adzamukhululukira mkaziyo. 13 Pa nkhani yokhudza lonjezo lililonse kapena lumbiro lokhudza kudzimana kapenanso kulolera kuvutika, mwamuna wake ali ndi mphamvu zovomereza kapena kukana kuti mkaziyo akwaniritse lonjezolo. 14 Koma ngati mwamunayo sanatsutse zimene mkazi wakeyo walonjeza, masiku nʼkumapita, ndiye kuti mwamunayo wavomereza malonjezo onse a mkaziyo kapena malumbiro onse odzimana amene mkaziyo anachita. Iye wavomereza chifukwa sanamukanize mkaziyo pa tsiku limene anamva akulonjeza. 15 Koma ngati mwamunayo wafafaniza malonjezowo patapita nthawi kuchokera pa tsiku limene anamva malonjezowo, mwamunayo ndi amene aziyankha mlandu mʼmalo mwa mkazi wakeyo.+
16 Awa ndi malamulo amene Yehova anapatsa Mose okhudza mwamuna ndi mkazi wake, ndiponso bambo ndi mwana wake wachitsikana amene akukhala mʼnyumba mwake.”
31 Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti: 2 “Uwabwezere+ Amidiyani chifukwa cha zimene anachitira Aisiraeli.+ Pambuyo pake udzaikidwa mʼmanda ngati mmene anachitira ndi makolo ako.”*+
3 Choncho Mose analankhula ndi anthuwo kuti: “Konzekeretsani amuna pakati panu kuti apite kukamenyana* ndi Amidiyani, ndipo mukapereke chilango cha Yehova kwa Amidiyaniwo pobwezera zimene anachita. 4 Mutenge amuna 1,000 pa fuko lililonse la mafuko onse a Isiraeli kuti apite kunkhondo.” 5 Choncho kuchokera pa anthu masauzande a Aisiraeliwo,+ anatenga amuna 1,000 pa fuko lililonse. Amuna onse opita kunkhondo* anakwana 12,000.
6 Ndiyeno Mose anatumiza amunawo kunkhondo, amuna 1,000 pa fuko lililonse. Anawatumiza limodzi ndi Pinihasi,+ mwana wa wansembe Eleazara. Pinihasi ananyamula ziwiya zopatulika ndi malipenga operekera zizindikiro.+ 7 Amunawo anakamenyana ndi Amidiyani, mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose, ndipo anapha mwamuna aliyense. 8 Anthu amene anaphedwawo akuphatikizapo mafumu 5 a Chimidiyani. Mafumuwo anali Evi, Rekemu, Zuri, Hura ndi Reba. Komanso anapha Balamu+ mwana wa Beori ndi lupanga. 9 Koma Aisiraeli anagwira akazi a Chimidiyani ndi ana awo nʼkuwatenga kupita nawo kwawo. Anatenganso ziweto zawo zonse ndi chuma chawo chonse. 10 Mizinda yawo yonse imene ankakhala komanso misasa yawo yonse* anaiwotcha ndi moto. 11 Anatenga zinthu zawo zonse, kuphatikizapo anthu ndi ziweto zomwe. 12 Kenako anatenga anthu amene anawagwirawo limodzi ndi zinthu zina zonse nʼkupita nawo kwa Mose, wansembe Eleazara ndi kugulu la Aisiraeli, kumsasa wawo umene unali mʼchipululu cha Mowabu,+ pafupi ndi mtsinje wa Yorodano, ku Yeriko.
13 Atafika nawo kumeneko, Mose ndi wansembe Eleazara, limodzi ndi atsogoleri onse a anthuwo, anatuluka kukakumana nawo kunja kwa msasa. 14 Koma Mose anakwiya kwambiri ndi amuna amene ankatsogolera asilikaliwo, atsogoleri a magulu a asilikali 1,000 ndi atsogoleri a magulu a asilikali 100, amene ankachokera kunkhondo. 15 Mose anawafunsa kuti: “Kodi akazi onse mwawasiya amoyo? 16 Pajatu akazi amenewa ndi amene anatsatira mawu a Balamu nʼkunyengerera Aisiraeli kuti achimwire Yehova+ pa zimene zinachitika ku Peori,+ moti mliri unagwera gulu la anthu a Yehova.+ 17 Tsopano iphani mwana wamwamuna aliyense pakati pa anawa, ndiponso muphe mkazi aliyense amene anagonapo ndi mwamuna. 18 Koma ana aakazi onse aangʼono amene sanagonepo ndi mwamuna musawaphe.+ 19 Mumange msasa kunja kwa msasawu, ndipo mukhalemo masiku 7. Aliyense amene wapha munthu komanso aliyense amene wakhudza mtembo wa munthu wophedwa,+ adziyeretse+ pa tsiku lachitatu ndi pa tsiku la 7. Mudziyeretse limodzinso ndi anthu amene mwawagwirawo. 20 Muyeretse chovala chilichonse, chinthu chilichonse chachikopa, chilichonse chopangidwa ndi ubweya wa mbuzi komanso chilichonse chopangidwa ndi mtengo.”
21 Tsopano wansembe Eleazara anauza asilikali amene anapita kunkhondo aja kuti: “Tamverani zimene Yehova analamula Mose, 22 ‘Zinthu zagolide, zasiliva, zakopa, zachitsulo, zatini ndi zamtovu, 23 chilichonse chimene sichingapse ndi moto, chidutse pamoto kuti chikhale choyera. Kenako muzichiyeretsanso ndi madzi.+ Koma chilichonse chimene chingapse ndi moto muzichiyeretsa ndi madzi. 24 Mudzachape zovala zanu pa tsiku la 7 kuti mudzakhale oyera, pambuyo pake mudzalowe mumsasa.’”+
25 Kenako Yehova anauza Mose kuti: 26 “Iweyo ndi wansembe Eleazara ndi atsogoleri a gululo, muwerenge zinthu zonse zimene akatenga kunkhondo. Muwerenge anthu ndi ziweto zomwe. 27 Zinthuzo muzigawe pawiri. Hafu iperekedwe kwa asilikali omwe anapita kunkhondo, ndipo hafu inayo iperekedwe kwa gulu lonse la anthuwo.+ 28 Pa zinthu zimene zaperekedwa kwa asilikali omwe anapita kunkhondo, mutengepo chamoyo chimodzi pa zamoyo 500 zilizonse, pa anthu, ngʼombe, abulu ndi nkhosa kuti zikhale msonkho woperekedwa kwa Yehova. 29 Zimenezi muzitenge pa hafu imene iwo alandire, ndipo muzipereke kwa wansembe Eleazara monga chopereka kwa Yehova.+ 30 Pa hafu imene Aisiraeli alandira, mutengepo chamoyo chimodzi pa zamoyo 50 zilizonse, pa anthu, ngʼombe, abulu, nkhosa ndi pa ziweto zamtundu uliwonse. Muzipereke kwa Alevi,+ amene amagwira ntchito zokhudzana ndi utumiki wapachihema cha Yehova.”+
31 Choncho Mose ndi wansembe Eleazara anachita mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose. 32 Pa zinthu zonse zimene anthu amene anapita kunkhondowo anabweretsa panali nkhosa 675,000, 33 ngʼombe 72,000 34 ndi abulu 61,000. 35 Akazi amene anali asanagonepo ndi mwamuna+ analipo 32,000. 36 Pa hafu imene inaperekedwa kwa amuna omwe anapita kunkhondo panali nkhosa 337,500. 37 Nkhosa zimene anazipereka kwa Yehova monga msonkho zinalipo 675. 38 Ngʼombe zinalipo 36,000, ndipo pa ngʼombe zimenezi, 72 anazipereka kwa Yehova monga msonkho. 39 Abulu analipo 30,500, ndipo 61 anawapereka kwa Yehova monga msonkho. 40 Anthu analipo 16,000, ndipo 32 anaperekedwa kwa Yehova monga msonkho. 41 Ndiyeno Mose anapereka msonkhowo kwa wansembe Eleazara+ ngati chopereka kwa Yehova, mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose.
42 Pa hafu imene Mose anapereka kwa Aisiraeli, ya zinthu zimene anthu anabweretsa kuchokera kunkhondo, 43 panali nkhosa zokwana 337,500, 44 ngʼombe 36,000, 45 abulu 30,500, 46 ndipo anthu analipo 16,000. 47 Ndiyeno pa hafu imene anapereka kwa Aisiraeliwo, Mose anatengapo chamoyo chimodzi pa zamoyo 50 zilizonse, pa anthu ndi pa ziweto. Zinthu zimenezi anazipereka kwa Alevi+ amene ankatumikira pachihema cha Yehova,+ mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose.
48 Kenako atsogoleri a masauzande a asilikali+ anafika kwa Mose. Iwowa anali atsogoleri a magulu a asilikali 1,000 ndi atsogoleri a magulu a asilikali 100. 49 Iwo anauza Mose kuti: “Ife atumiki anu tawerenga amuna onse ankhondo amene tikuwayangʼanira, ndipo palibe ndi mmodzi yemwe amene akusowapo.+ 50 Choncho tiloleni kuti aliyense wa ife apereke zinthu zimene wabwera nazo monga chopereka kwa Yehova. Tabwera ndi zinthu zagolide, matcheni ovala mʼmiyendo, zibangili, mphete zachifumu, ndolo ndi zodzikongoletsera zina. Tipereka zimenezi kwa Yehova kuti ziphimbe machimo athu.”
51 Choncho Mose ndi wansembe Eleazara analandira golideyo kwa iwo, kutanthauza zodzikongoletsera zonse zamtengo wapatali. 52 Golide yense amene anamupereka kwa Yehova anakwana masekeli* 16,750. Ameneyu ndi golide amene atsogoleri a magulu a asilikali 1,000 komanso atsogoleri a magulu a asilikali 100 anapereka. 53 Aliyense wa amuna amene anapita kunkhondowo anabwerako ndi zinthu. 54 Choncho Mose ndi wansembe Eleazara analandira zinthu zagolidezo kwa atsogoleri a magulu a asilikali 1,000, ndiponso kwa atsogoleri a magulu a asilikali 100. Ndipo zinthu zagolidezo anakaziika mʼchihema chokumanako, kuti zikhale chikumbutso kwa Aisiraeli pamaso pa Yehova.
32 Tsopano ana a Rubeni+ ndi ana a Gadi+ anali ndi ziweto zambiri ndipo anaona kuti dera la Yazeri+ komanso la Giliyadi, anali malo abwino a ziweto. 2 Choncho ana a Gadi ndi ana a Rubeniwo anapita kwa Mose, wansembe Eleazara ndi atsogoleri a gululo, nʼkukawauza kuti: 3 “Ataroti, Diboni, Yazeri, Nimira, Hesiboni,+ Eleyale, Sebamu, Nebo+ komanso Beoni,+ 4 ndi madera amene Yehova anawagonjetsa kuti akhale a Aisiraeli.+ Madera amenewa ndi abwino kwa ziweto, ndipo atumiki anufe tili ndi ziweto zambiri.”+ 5 Anapitiriza kuti: “Ngati mungatikomere mtima atumiki anufe, mutipatse madera amenewa kuti akhale cholowa chathu. Tisawoloke nawo Yorodano.”
6 Koma Mose poyankha, anafunsa ana a Gadi ndi ana a Rubeniwo kuti: “Kodi mukufuna kuti abale anu apite kunkhondo inu mutatsala kuno? 7 Nʼchifukwa chiyani mukufuna kufooketsa Aisiraeli kuti asawolokere kudziko limene Yehova anatsimikiza mtima kuwapatsa? 8 Nʼzimenenso makolo anu anachita ku Kadesi-barinea, nditawatuma kuti akafufuze dziko.+ 9 Iwo atafika kuchigwa cha Esikolo*+ nʼkuliona dzikolo, anafooketsa Aisiraeli kuti asakalowe mʼdziko limene Yehova anatsimikiza mtima kuwapatsa.+ 10 Pa tsiku limenelo Yehova anakwiya koopsa, ndipo analumbira kuti:+ 11 ‘Amuna amene anatuluka mu Iguputo kuyambira azaka 20 kupita mʼtsogolo, sadzaliona dziko+ limene ndinalumbira kuti ndidzapereka kwa Abulahamu, Isaki ndi Yakobo,+ chifukwa sanandimvere ndi mtima wonse. 12 Koma Kalebe+ mwana wa Yefune Mkenizi, ndi Yoswa+ mwana wa Nuni, adzaliona dzikolo chifukwa akhala akumvera Yehova ndi mtima wonse.’+ 13 Yehova anawakwiyira koopsa Aisiraeli ndipo anawachititsa kuti azingoyendayenda mʼchipululu kwa zaka 40,+ mpaka mʼbadwo wonse wochita zoipa pamaso pa Yehova utatha.+ 14 Inunso mukuchita zoipa mofanana ndi makolo anu, ndipo mukuchititsa kuti mkwiyo woyaka moto wa Yehova uwonjezeke pa Isiraeli. 15 Mukasiya kumumvera, ndithu iye adzachititsanso anthu onsewa kukhalabe mʼchipululu muno ndipo mudzachititsa kuti anthu onsewa azunzike kwambiri.”
16 Kenako iwo anapitanso kwa iye nʼkunena kuti: “Mutilole timange makola amiyala a ziweto zathu kunoko ndi mizinda ya ana athu. 17 Koma ifeyo tikonzeka kuti tikamenye nkhondo+ ndipo tikhala patsogolo pa Aisiraeli mpaka titakawafikitsa kumalo awo. Koma ana athu tiwasiya mʼmizinda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri kuti tiwateteze kwa anthu a dziko lino. 18 Sitidzabwerera kunyumba zathu mpaka aliyense wa Aisiraeli atalandira malo ake kuti akhale cholowa chake.+ 19 Ife sitidzalandira nawo cholowa tsidya ilo la Yorodano kupita kutsogoloko, chifukwa talandira cholowa chathu kutsidya lakumʼmawa kwa Yorodano.”+
20 Mose anawauza kuti: “Chabwino, koma zitheka ngati mutachita izi: Mutenge zida nʼkukamenya nkhondo pamaso pa Yehova.+ 21 Komanso ngati aliyense wa inu atatenga zida zake zankhondo nʼkuwoloka Yorodano pamaso pa Yehova, mpaka atathamangitsa adani ake pamaso pake,+ 22 ndiponso mpaka dzikolo litagonjetsedwa pamaso pa Yehova.+ Pambuyo pake mukhoza kudzabwerera+ ndipo mudzakhala opanda mlandu kwa Yehova ndi kwa Isiraeli. Kenako dzikoli lidzakhala lanu pamaso pa Yehova.+ 23 Koma mukapanda kuchita zimenezi, mudzakhala kuti mwachimwira Yehova. Ndipo mukatero, dziwani kuti tchimo lanu lidzakutsatani. 24 Ndiye mukhoza kumanga mizinda ya ana anu ndi makola a ziweto zanu.+ Koma muchitedi zimene mwalonjeza.”
25 Ana a Gadi ndi ana a Rubeni anayankha Mose kuti: “Ife atumiki anu tichita zonse zimene mwalamula mbuyathu. 26 Ana athu ndi akazi athu atsala kuno mʼmizinda ya Giliyadi,+ limodzi ndi ziweto zathu zonse. 27 Koma atumiki anufe tiwoloka, aliyense atatenga zida kukamenya nkhondo pamaso pa Yehova,+ mogwirizana ndi zimene mwanena mbuyathu.”
28 Choncho Mose anapereka lamulo lokhudza iwowo kwa wansembe Eleazara, Yoswa mwana wa Nuni ndi kwa atsogoleri a mafuko a Isiraeli. 29 Iye anawauza kuti: “Ngati ana a Gadi ndi ana a Rubeni atawoloka nanu Yorodano, aliyense atatenga zida kuti akamenye nkhondo pamaso pa Yehova, nʼkugonjetsa dzikolo pamaso panu, mudzawapatse dziko la Giliyadi kuti likhale cholowa chawo.+ 30 Koma akapanda kutenga zida nʼkuwoloka nanu limodzi, basi azidzakhala pakati panu mʼdziko la Kanani.”
31 Ana a Gadi ndi ana a Rubeni atamva mawuwo anati: “Tidzachita zimene Yehova walankhula kwa atumiki anufe. 32 Tidzawoloka ndi zida kukamenya nkhondo pamaso pa Yehova kudziko la Kanani.+ Koma tidzalandira cholowa chathu tsidya lino la Yorodano.” 33 Choncho Mose anapereka malo kwa ana a Gadi, ana a Rubeni+ komanso hafu ya fuko la Manase+ mwana wa Yosefe. Anawapatsa malo a ufumu wa Sihoni+ mfumu ya Aamori, malo a ufumu wa Ogi+ mfumu ya Basana ndi dera lonse la mizinda komanso midzi yozungulira.
34 Ndipo ana a Gadi anamanga* mizinda ya Diboni,+ Ataroti,+ Aroweli,+ 35 Atiroti-sofani, Yazeri,+ Yogebeha,+ 36 Beti-nimira+ ndi Beti-harana.+ Mizinda imeneyi inali ndi mipanda yolimba kwambiri komanso inali ndi makola a ziweto amiyala. 37 Ana a Rubeni anamanga mizinda ya Hesiboni,+ Eleyale,+ Kiriyataimu,+ 38 Nebo,+ Baala-meoni,+ ndi Sibima. Mayina a mizindayi anawasintha, nʼkuipatsa mayina ena atsopano.
39 Ana a Makiri+ mwana wa Manase, anaukira mzinda wa Giliyadi nʼkuulanda ndipo anathamangitsa Aamori amene ankakhala mumzindawo. 40 Choncho Mose anapereka mzinda wa Giliyadi kwa Makiri mwana wa Manase, ndipo iye anayamba kukhala mmenemo.+ 41 Yairi mwana wa Manase anaukira Aamori nʼkulanda midzi yawo ingʼonoingʼono. Midzi imeneyi anayamba kuitchula kuti Havoti-yairi.*+ 42 Noba nayenso anaukira nʼkulanda mzinda wa Kenati ndi midzi yake yozungulira. Mzindawo anaupatsa dzina lake, loti Noba.
33 Awa ndi malo amene Aisiraeli ankaima pa ulendo wawo, atatuluka mʼdziko la Iguputo+ mʼmagulu awo*+ motsogoleredwa ndi Mose komanso Aroni.+ 2 Mose ankalemba malo amene ankanyamukira ulendo uliwonse mogwirizana ndi zimene Yehova anamulamula. Awa ndi maulendo amene anayenda kuchokera kumalo ena kukafika kumalo ena:+ 3 Ananyamuka ku Ramese+ mʼmwezi woyamba, pa tsiku la 15.+ Tsiku lotsatira atachita Pasika,+ Aisiraeli ananyamuka molimba mtima* pamaso pa Aiguputo onse. 4 Pa nthawiyi nʼkuti Aiguputo ali pa ntchito yoika mʼmanda ana onse oyamba kubadwa,+ amene Yehova anawapha pakati pawo. Yehovayo anali atapereka ziweruzo pa milungu yawo.+
5 Ndiyeno Aisiraeli ananyamuka ku Ramese nʼkukamanga msasa ku Sukoti.+ 6 Kenako ananyamuka ku Sukoti nʼkukamanga msasa ku Etamu,+ pafupi ndi chipululu. 7 Atanyamuka ku Etamu anabwerera mʼmbuyo kulowera ku Pihahiroti amene anali moyangʼanizana ndi Baala-zefoni.+ Ndipo anakamanga msasa pafupi ndi Migidoli.+ 8 Pambuyo pake ananyamuka ku Pihahiroti, nʼkukadutsa panyanja+ kuwolokera kuchipululu.+ Anayenda ulendo wamasiku atatu mʼchipululu cha Etamu,+ nʼkukamanga msasa ku Mara.+
9 Kenako ananyamuka ku Mara nʼkukafika ku Elimu. Ku Elimuko kunali akasupe 12 a madzi komanso mitengo 70 ya kanjedza, ndipo anamanga msasa kumeneko.+ 10 Atachoka ku Elimu, anakamanga msasa pafupi ndi Nyanja Yofiira. 11 Atanyamuka ku Nyanja Yofiira, anakamanga msasa mʼchipululu cha Sini.+ 12 Kenako ananyamuka mʼchipululu cha Sini, nʼkukamanga msasa ku Dofika. 13 Atachoka ku Dofika, anakamanga msasa ku Alusi. 14 Atanyamuka ku Alusi, anakamanga msasa ku Refidimu,+ kumene kunalibe madzi oti anthu amwe. 15 Pambuyo pake anachoka ku Refidimu nʼkukamanga msasa mʼchipululu cha Sinai.+
16 Kenako ananyamuka mʼchipululu cha Sinai, nʼkukamanga msasa ku Kibiroti-hatava.+ 17 Atachoka ku Kibiroti-hatava, anakamanga msasa ku Hazeroti.+ 18 Pambuyo pake ananyamuka ku Hazeroti nʼkukamanga msasa ku Ritima. 19 Atachoka ku Ritima anakamanga msasa ku Rimoni-perezi. 20 Atanyamuka ku Rimoni-perezi, anakamanga msasa ku Libina. 21 Kenako anachoka ku Libina nʼkukamanga msasa ku Risa. 22 Atanyamuka ku Risa, anakamanga msasa ku Kehelata. 23 Atachoka ku Kehelata, anakamanga msasa kuphiri la Saferi.
24 Pambuyo pake ananyamuka kuphiri la Saferi, nʼkukamanga msasa ku Harada. 25 Atachoka ku Harada, anakamanga msasa ku Makeloti. 26 Atanyamuka+ ku Makeloti, anakamanga msasa ku Tahati. 27 Atachoka ku Tahati, anakamanga msasa ku Tera. 28 Kenako ananyamuka ku Tera nʼkukamanga msasa ku Mitika. 29 Pambuyo pake anachoka ku Mitika nʼkukamanga msasa ku Hasimona. 30 Atanyamuka ku Hasimona anakamanga msasa ku Mosera. 31 Kenako ananyamuka ku Mosera nʼkukamanga msasa ku Bene-yaakana.+ 32 Atachoka ku Bene-yaakana anakamanga msasa ku Hori-hagidigadi. 33 Atanyamuka ku Hori-hagidigadi anakamanga msasa ku Yotibata.+ 34 Pambuyo pake ananyamuka ku Yotibata nʼkukamanga msasa ku Abirona. 35 Kenako anachoka ku Abirona nʼkukamanga msasa ku Ezioni-geberi.+ 36 Atanyamuka ku Ezioni-geberi anakamanga msasa mʼchipululu cha Zini,+ ku Kadesi.
37 Pambuyo pake ananyamuka ku Kadesi, nʼkukamanga msasa kuphiri la Hora,+ kumalire ndi dziko la Edomu. 38 Wansembe Aroni anakwera mʼphiri la Hora mogwirizana ndi zimene Yehova analamula, ndipo anamwalira mʼphirimo mʼchaka cha 40 mʼmwezi wa 5 pa tsiku loyamba la mweziwo kuchokera pamene Aisiraeli anatuluka mʼdziko la Iguputo.+ 39 Aroni anamwalira mʼphiri la Hora ali ndi zaka 123.
40 Tsopano mfumu ya ku Aradi+ ya Chikanani, imene inkakhala ku Negebu mʼdziko la Kanani, inamva kuti Aisiraeli akubwera.
41 Patapita nthawi Aisiraeli ananyamuka kuphiri la Hora,+ nʼkukamanga msasa ku Tsalimona. 42 Pambuyo pake anachoka ku Tsalimona, nʼkukamanga msasa ku Punoni. 43 Kenako ananyamuka ku Punoni nʼkukamanga msasa ku Oboti.+ 44 Atachoka ku Oboti anakamanga msasa ku Iye-abarimu, kumalire ndi Mowabu.+ 45 Kenako ananyamuka ku Iyimu* nʼkukamanga msasa ku Diboni-gadi.+ 46 Pambuyo pake ananyamuka ku Diboni-gadi, nʼkukamanga msasa ku Alimoni-dibilataimu. 47 Kenako ananyamuka ku Alimoni-dibilataimu, nʼkukamanga msasa kumapiri a Abarimu,+ pafupi ndi Nebo.+ 48 Potsirizira pake ananyamuka kumapiri a Abarimu nʼkukamanga msasa ku Yeriko, pafupi ndi mtsinje wa Yorodano, mʼchipululu cha Mowabu.+ 49 Anapitiriza kukhala mumsasa pafupi ndi Yorodano, kuyambira ku Beti-yesimoti mpaka ku Abele-sitimu,+ mʼchipululu cha Mowabu.
50 Yehova analankhula ndi Mose ku Yeriko, pafupi ndi mtsinje wa Yorodano, mʼchipululu cha Mowabu. Anamuuza kuti: 51 “Lankhula ndi Aisiraeli, uwauze kuti, ‘Tsopano muwoloka Yorodano kuti mulowe mʼdziko la Kanani.+ 52 Mukathamangitse anthu onse amene akukhala mʼdzikolo, ndipo mukawononge zifaniziro zawo zonse zamiyala+ ndi mafano awo onse achitsulo*+ komanso mukagwetse malo awo onse opatulika.+ 53 Mukalande dzikolo kuti muzikakhalamo, chifukwa ndidzalipereka ndithu kwa inu kuti likhale lanu.+ 54 Mukagwiritse ntchito maere+ pogawa dzikolo kwa mabanja anu kuti likhale cholowa chanu. Banja la anthu ambiri mukaliwonjezere cholowa chawo, ndipo banja la anthu ochepa mukalichepetsere cholowa chawo.+ Banja lililonse mukalipatse cholowa mogwirizana ndi kumene maere a banjalo agwera. Mukalandira malo kuti akhale cholowa chanu potsata mafuko a makolo anu.+
55 Koma ngati simukathamangitsa anthu amene akukhala mʼdzikolo,+ anthu amene mukawasiyewo adzakhala ngati zitsotso mʼmaso mwanu, ndiponso ngati minga yokubayani mʼnthiti mwanu. Ndipo iwo azidzakuvutitsani mʼdziko limene muzidzakhala.+ 56 Zikadzatero, chilango chimene ndimafuna kupereka kwa anthuwo ndidzachipereka kwa inu.’”+
34 Yehova analankhulanso ndi Mose kuti: 2 “Upereke malangizo awa kwa Aisiraeli: ‘Awa ndi malire a dziko la Kanani, dziko limene ndidzakupatseni kuti likhale cholowa chanu.+
3 Malire a dziko lanu mbali yakumʼmwera adzayambire kuchipululu cha Zini, malire ndi Edomu. Malire anu akumʼmwera, mbali yakumʼmawa, adzayambire kumene Nyanja Yamchere* yathera.+ 4 Malirewo adzakhota nʼkukadutsa kumʼmwera kwa chitunda cha Akirabimu+ kulowera ku Zini, nʼkukathera kumʼmwera kwa Kadesi-barinea.+ Kenako akakhotere ku Hazara-adara+ nʼkukafika ku Azimoni. 5 Ndiyeno kuchokera ku Azimoni, malirewo akalowere kuchigwa cha Iguputo* mpaka kukathera ku Nyanja Yaikulu.*+
6 Malire anu a mbali yakumadzulo akakhale gombe la Nyanja Yaikulu.* Amenewa akakhale malire anu a mbali yakumadzulo.+
7 Malire anu akumpoto akayende motere: Mukalembe malirewo kuchokera ku Nyanja Yaikulu mpaka kuphiri la Hora.+ 8 Kuchokera kuphiri la Hora, mukalembe malirewo mpaka kukafika ku Lebo-hamati,*+ ndipo malirewo akathere ku Zedadi.+ 9 Malirewo akafike ku Zifironi, mpaka kukathera ku Hazara-enani.+ Malire anu a mbali yakumpoto akakhale amenewa.
10 Ndiyeno mukalembe malire anu a kumʼmawa kuyambira ku Hazara-enani mpaka ku Sefamu. 11 Malirewo akatsike kuchokera ku Sefamu kulowera ku Ribila, kumʼmawa kwa Aini. Akatsikebe mpaka akadutse pamalo otsetsereka akumʼmawa kwa Nyanja ya Kinereti.*+ 12 Malirewo akatsike ndithu mpaka kumtsinje wa Yorodano, ndipo akathere ku Nyanja Yamchere.+ Limeneli ndi limene lidzakhale dziko lanu+ ndi malire ake olizungulira.’”
13 Choncho Mose anauza Aisiraeli kuti: “Limeneli ndi dziko limene ligawidwe kwa inu pogwiritsa ntchito maere kuti likhale cholowa chanu.+ Lidzagawidwa kwa inu mogwirizana ndi zimene Yehova analamula kuti liperekedwe kwa mafuko 9 ndi hafu. 14 Fuko la Rubeni potengera mabanja a makolo awo, fuko la Gadi potengera mabanja a makolo awo komanso hafu ya fuko la Manase, analandira kale cholowa chawo.+ 15 Mafuko awiri ndi hafuwo analandira kale cholowa chawo kudera lakumʼmawa kwa Yorodano, moyangʼanizana ndi Yeriko.”+
16 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 17 “Amuna amene akakugawireni malo kuti akhale cholowa chanu, mayina awo ndi awa: Wansembe Eleazara+ ndi Yoswa+ mwana wa Nuni. 18 Mutenge mtsogoleri mmodzi pa fuko lililonse kuti akathandize kugawa malowo kuti akhale cholowa chanu.+ 19 Amunawo mayina awo ndi awa: pa fuko la Yuda,+ Kalebe+ mwana wa Yefune, 20 pa fuko la ana a Simiyoni,+ Semuyeli mwana wa Amihudi, 21 pa fuko la Benjamini,+ Elidadi mwana wa Kisiloni, 22 pa fuko la ana a Dani,+ mtsogoleri Buki mwana wa Yogili, 23 pa ana a Yosefe+ ku fuko la ana a Manase,+ mtsogoleri Hanieli mwana wa Efodi, 24 pa fuko la ana a Efuraimu,+ mtsogoleri Kemueli mwana wa Sipitana, 25 pa fuko la ana a Zebuloni,+ mtsogoleri Elizafana mwana wa Paranaki, 26 pa fuko la ana a Isakara,+ mtsogoleri Palitiyeli mwana wa Azani, 27 pa fuko la ana a Aseri,+ mtsogoleri Ahihudi mwana wa Selomi, 28 ndipo pa fuko la ana a Nafitali,+ mtsogoleri Pedaheli mwana wa Amihudi.” 29 Amenewa ndi amuna amene Yehova anawalamula kuti akagawe malo kwa Aisiraeli mʼdziko la Kanani.+
35 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose mʼchipululu cha Mowabu ku Yeriko, pafupi ndi mtsinje wa Yorodano+ kuti: 2 “Lamula Aisiraeli kuti pacholowa chawo cha malo, akapereke kwa Alevi mizinda yokhalamo.+ Akaperekenso kwa Aleviwo malo odyetserako ziweto ozungulira mizindayo.+ 3 Aleviwo azikakhala mʼmizindayo, ndipo malo odyetserako ziwetowo akakhala a ziweto zawo, katundu wawo ndi nyama zawo zonse. 4 Malo odyetserako ziweto a mizinda imene mukapereke kwa Aleviwo, akakhale mamita 445* kuchokera pampanda wa mzindawo kuzungulira mzinda wonse. 5 Mukayeze kunja kwa mzinda, mamita 890 kumbali yakumʼmawa, mamita 890 kumbali yakumʼmwera, mamita 890 kumbali yakumadzulo, ndi mamita 890 kumbali yakumpoto, kuzungulira mzinda. Amenewa akakhale malo odyetserako ziweto kwa anthu amʼmizindayo.
6 Mukapereke kwa Alevi mizinda 6 yoti munthu amene wapha mnzake azikathawirako. Kuwonjezera pa mizindayi, mukapereke kwa Aleviwo mizinda ina 42.+ 7 Mizinda yonse imene mukapereke kwa Alevi ikakwane 48. Mizindayi mukawapatse limodzi ndi malo ake odyetserako ziweto.+ 8 Mizinda imene mukawapatseyo ikachokere pa cholowa cha Aisiraeli.+ Pa fuko lalikulu mukatenge mizinda yambiri, ndipo pa fuko lalingʼono mukatenge yochepa.+ Fuko lililonse likapereke ina ya mizinda yake kwa Alevi mogwirizana ndi cholowa chimene akalandire.”
9 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 10 “Lankhula ndi Aisiraeli, uwauze kuti, ‘Muwoloka Yorodano kupita kudziko la Kanani.+ 11 Mukasankhe mizinda yoyenerera kwa inu, kuti ikakhale mizinda yanu yothawirako. Munthu amene wapha mnzake mwangozi azikathawira kumeneko.+ 12 Mizindayo ikakhale malo amene munthu wopha mnzake, amene akuthawa wobwezera magazi+ azikathawirako, kuti amene wapha mnzakeyo asaphedwe mpaka mlandu wake utaweruzidwa pamaso pa oweruza.+ 13 Mizinda yothawirako 6 imene mukaperekeyo, izikagwira ntchito imeneyi. 14 Mupereke mizinda itatu tsidya lino la Yorodano,+ ndiponso mukapereke mizinda itatu tsidya linalo, mʼdziko la Kanani.+ Imeneyi ikakhala mizinda yothawirako. 15 Mizinda 6 imeneyi ikakhale kothawirako Aisiraeli, mlendo+ komanso munthu aliyense amene akukhala pakati pawo, aliyense amene wapha munthu mwangozi.+
16 Koma ngati munthu wamenya mnzake ndi chitsulo nʼkufa, ameneyo ndi wopha munthu. Ndipo wopha munthuyo ayenera kuphedwa ndithu.+ 17 Ngati wagenda mnzake ndi mwala woti ungaphe munthu, mnzakeyo nʼkufa, ameneyo ndi wopha munthu. Ndipo wopha munthuyo aphedwe ndithu. 18 Ngati wamenya mnzake ndi mtengo woti ungaphe munthu, mnzakeyo nʼkufa, ameneyo ndi wopha munthu. Wopha munthuyo aphedwe ndithu.
19 Wobwezera magazi ndi amene ayenera kupha munthu amene wapha mnzakeyo. Akadzangomupeza, wobwezera magaziyo adzamuphe. 20 Ngati munthu wafa wina atamukankha chifukwa chodana naye, kapena ngati wafa wina atamugenda ndi chinachake ndi zolinga zoipa,*+ 21 kapenanso wafa wina atamumenya ndi dzanja lake chifukwa chodana naye, amene wapha mnzakeyo aphedwe ndithu. Iye ndi wopha munthu. Wobwezera magazi aphe wopha munthuyo akangomupeza.
22 Koma ngati wamukankha mwangozi, osati chifukwa choti amadana naye, kapena ngati wamugenda ndi chinachake mwangozi, osati ndi zolinga zoipa,*+ 23 kapena ngati samamuona ndipo wamugwetsera mwala, mnzakeyo nʼkufa, koma sanali mdani wake komanso analibe cholinga choti amuvulaze, 24 oweruza aweruze pakati pa wopha mnzakeyo ndi woyenera kubwezera magaziyo, mogwirizana ndi malamulo amenewa.+ 25 Kenako oweruzawo azipulumutsa wopha munthuyo mʼmanja mwa wobwezera magazi, ndipo amubwezere kumzinda wothawirako kumene anathawira. Iye ayenera kukhala mumzindamo mpaka mkulu wa ansembe amene anadzozedwa ndi mafuta opatulika adzamwalire.+
26 Koma wopha munthuyo akatuluka kunja kwa malire a mzinda wothawirako kumene anathawira, 27 wobwezera magazi nʼkumupeza kunja kwa malire a mzinda wothawirako nʼkumupha, wobwezera magaziyo alibe mlandu wa magazi. 28 Wopha munthuyo ayenera kukhala mumzinda wothawirako mpaka mkulu wa ansembe atamwalira. Pambuyo pa imfa ya mkulu wa ansembe, wopha munthuyo akhoza kubwerera kumalo a cholowa chake.+ 29 Amenewa adzakhale malamulo anu oweruzira milandu mʼmibadwo yanu yonse kulikonse kumene mukakhale.
30 Aliyense amene wapha munthu aziphedwa+ pambuyo poti mboni zatsimikizira.+ Koma munthu sakuyenera kuphedwa ngati pali umboni woperekedwa ndi munthu mmodzi yekha. 31 Musamalandire dipo lowombolera moyo wa munthu amene wapha mnzake, chifukwa ndi woyenera kuphedwa. Aphedwe ndithu ameneyo.+ 32 Komanso musamalandire dipo lowombolera munthu amene anathawira kumzinda wothawirako, nʼcholinga choti aloledwe kubwerera kwawo mkulu wa ansembe asanamwalire.
33 Musamadetse dziko limene mukukhalamo, chifukwa magazi ndi amene amadetsa dziko.+ Ndipo dziko limene ladetsedwa ndi magazi silingayeretsedwe ndi china chilichonse, kupatulapo magazi a munthu amene anakhetsa magaziyo.+ 34 Musamadetse dziko limene mukukhalamo, limene inenso ndikukhalamo, chifukwa ine Yehova ndikukhala pakati pa Aisiraeli.’”+
36 Atsogoleri a mabanja omwe anachokera mwa Giliyadi mwana wa Makiri,+ mwana wa Manase, ochokera kumabanja a ana a Yosefe, anapita kukalankhula ndi Mose komanso akalonga omwe anali atsogoleri a Aisiraeli. 2 Iwo anati: “Paja Yehova anakulamulani inu mbuyathu, kuti mugawe dzikoli pochita maere+ kuti likhale cholowa cha Aisiraeli. Yehova anakulamulaninso kuti mupereke cholowa cha mchimwene wathu Tselofekadi kwa ana ake aakazi.+ 3 Ngati ana aakaziwa atakwatiwa ndi amuna a mafuko ena a Aisiraeli, ndiye kuti cholowa chawo chidzachotsedwa ku cholowa cha makolo athu, ndipo chidzawonjezedwa ku cholowa cha fuko limene aliyense adzakwatiweko. Zikadzatero ndiye kuti cholowa chathu cha malo chidzachepa. 4 Ndiye chaka cha Ufulu+ cha Aisiraeli chikadzafika, cholowa cha akaziwa chidzachotsedwa ku cholowa cha fuko la makolo athu, ndipo chidzawonjezedwa ku cholowa cha fuko limene aliyense wa iwo adzakwatiweko ndipo chidzakhala cha fukolo mpaka kalekale.”
5 Ndiyeno Mose anauza Aisiraeli zimene Yehova anamuuza kuti: “Zimene fuko la ana a Yosefe likunena ndi zoona. 6 Zimene Yehova walamula zokhudza ana aakazi a Tselofekadi nʼzakuti: ‘Iwo angakwatiwe ndi aliyense amene angamukonde. Koma ayenera kukwatiwa ndi amuna a fuko la makolo awo okha. 7 Cholowa cha Aisiraeli chisamachotsedwe ku fuko lina kupita ku fuko lina. Aliyense wa Aisiraeli ayenera kusunga cholowa cha fuko la makolo ake. 8 Choncho, mwana wamkazi aliyense amene walandira nawo cholowa pakati pa mafuko a Aisiraeli, azikwatiwa ndi mwamuna wa mʼbanja la fuko la makolo ake,+ kuti aliyense wa Aisiraeli azisunga cholowa chochokera kwa makolo ake. 9 Cholowa chilichonse chisachotsedwe ku fuko lina kupita ku fuko lina. Fuko lililonse la Aisiraeli lizisunga cholowa chake.’”
10 Ana aakazi a Tselofekadi anachitadi zimene Yehova analamula Mose.+ 11 Choncho Mala, Tiriza, Hogila, Milika ndi Nowa, ana aakazi a Tselofekadi,+ anakwatiwa ndi ana a azichimwene a bambo awo. 12 Iwo anakwatiwa ndi amuna ochokera ku mabanja a ana a Manase mwana wa Yosefe, kuti cholowa chawo chisachoke ku fuko la banja la bambo awo.
13 Amenewa ndi malamulo ndi zigamulo za Yehova, zimene anapereka kwa Aisiraeli kudzera mwa Mose ku Yeriko, mʼchipululu cha Mowabu, pafupi ndi mtsinje wa Yorodano.+
Mʼchilankhulo choyambirira, “ana a Isiraeli.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mogwirizana ndi magulu awo a asilikali.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “potengera magulu awo a asilikali.”
Kapena kuti, “wolondera; wotumikira pa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mogwirizana ndi magulu awo a asilikali.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mogwirizana ndi magulu awo a asilikali.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mogwirizana ndi magulu awo a asilikali.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mogwirizana ndi magulu awo a asilikali.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mibadwo ya.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “amene manja awo anadzazidwa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Mlendo,” kutanthauza mwamuna amene si wa mʼbanja la Aroni.
Mʼchilankhulo choyambirira, “ana onse oyamba kubadwa, otsegula mimba ya mayi awo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Mlendo aliyense,” kutanthauza munthu amene si Mlevi.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Sekeli imodzi inali yofanana ndi magalamu 11.4. Onani Zakumapeto B14.
Kapena kuti, “mogwirizana ndi sekeli yoyera.”
Gera imodzi inali yofanana ndi magalamu 0.57. Onani Zakumapeto B14.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Kapena kuti “phulusa la mafuta,” kutanthauza phulusa losakanikirana ndi mafuta a nsembe.
Gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa efa ndi lofanana ndi malita 2.2. Onani Zakumapeto B14.
Kamzere kameneka kakusonyeza kuti mawuwa anathera mʼmalere.
Nʼkutheka kuti izi zikutanthauza kuti ankakhala wosabereka.
Zikuoneka kuti mawu akuti “ntchafu,” akuimira ziwalo zoberekera.
Nʼkutheka kuti izi zikutanthauza kuti ankakhala wosabereka.
Zikuoneka kuti mawu akuti “ntchafu,” akuimira ziwalo zoberekera.
Mʼchilankhulo choyambirira, “Ame! Ame!”
Zikuoneka kuti mawu akuti “ntchafu,” akuimira ziwalo zoberekera.
Nʼkutheka kuti izi zikutanthauza kuti ankakhala wosabereka.
MʼChiheberi na·zir′, kutanthauza “Wosankhidwa; Wodzipereka; Wopatulidwa.”
“Viniga” ndi chakumwa chowawasira chomwe chinkapangidwa kuchokera ku vinyo wosasa kapena zakumwa zina zoledzeretsa.
Sekeli imodzi inali yofanana ndi magalamu 11.4. Onani Zakumapeto B14.
Kapena kuti, “mogwirizana ndi sekeli yoyera.”
Kapena kuti, “mbale imodzi yaingʼono yolowa.”
Kapena kuti, “ana onse oyamba kubadwa, otsegula mimba ya mayi awo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “pakati pa madzulo awiri.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “pakati pa madzulo awiri.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “pakati pa madzulo awiri.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mogwirizana ndi magulu awo ankhondo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mogwirizana ndi magulu awo ankhondo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mogwirizana ndi magulu awo ankhondo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mogwirizana ndi magulu awo ankhondo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mogwirizana ndi magulu awo ankhondo.”
Kapena kuti, Yetero.
Kapena kuti, “mungakhale maso athu.”
Kapena kuti, “kwa Aisiraeli miyandamiyanda.”
Dzina limeneli limatanthauza “Kuyaka; moto walawilawi.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “njere ya koriyanda.” Koriyanda ndi chomera chimene ena amati “masala,” ndipo njere yake ndi yoyera ngati mapira.
Kapena kuti, “amene ukuwadziwa.”
Kapena kuti, “anayamba kunenera.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mikono iwiri.” Onani Zakumapeto B14.
Homeri imodzi inali yofanana ndi malita 220. Onani Zakumapeto B14.
Kutanthauza kuti, “Manda a Anthu Adyera.”
Kapena kuti, “anali wodzichepetsa kwambiri kuposa munthu aliyense.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Iye wasonyeza kuti ndi wokhulupirika mʼnyumba mwanga monse.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “pakamwamʼpakamwa.”
Kapena kuti, “akafufuze.”
Kapena kuti, “Yehoswa,” kutanthauza kuti “Yehova Ndi Chipulumutso.”
Kapena kuti, “polowera ku Hamati.”
Aanaki anali anthu amatupi akuluakulu komanso amphamvu kwambiri.
Kapena kuti, “kukhwawa la Esikolo.”
“Makangaza” ndi mtundu wa chipatso. Ena amati chimanga chachizungu.
Kapena kuti, “kukhwawa la Esikolo.” Dzinali limatanthauza “Phava la Mphesa.”
Nʼkutheka kuti dzinali limatanthauza “Ogwetsa” kutanthauza amene amagwetsa anthu ena. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mʼchilankhulo choyambirira, “ngati munthu mmodzi.”
Kapena kuti, “amasonyeza kukoma mtima kosatha.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “anali ndi mzimu wosiyana ndi ena.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ndinakweza dzanja langa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “uhule wanu.”
Kapena kuti, “kondiona ngati mdani.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “kafungo kokhazika mtima pansi.”
Gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa efa ndi lofanana ndi malita 2.2. Onani Zakumapeto B14.
Muyezo wa hini ndi wofanana ndi malita 3.67. Onani Zakumapeto B14.
Mʼchilankhulo choyambirira, “yakafungo kokhazika mtima pansi.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “kafungo kokhazika mtima pansi.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “kafungo kokhazika mtima pansi.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “kafungo kokhazika mtima pansi.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “yakafungo kokhazika mtima pansi.”
Komwe ndi kuchita uhule wauzimu, kapena kulambira milungu ina.
Mʼchilankhulo choyambirira, “Mulungu wa mizimu ya zamoyo zonse.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “si zamumtima mwanga.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “itsegule pakamwa pake.”
Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mʼchilankhulo choyambirira, “inatsegula pakamwa pake.”
Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mʼchilankhulo choyambirira, “mlendo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mlendo,” kutanthauza mwamuna amene si wa mʼbanja la Aroni.
Mʼchilankhulo choyambirira, “mlendo,” kutanthauza mwamuna amene si wa mʼbanja la Aroni.
Kutanthauza chilichonse chimene achipanga kuti chikhale chopatulika pochipereka kwa Mulungu moti sichingawomboledwenso mpaka kalekale.
Sekeli imodzi inali yofanana ndi magalamu 11.4. Onani Zakumapeto B14.
Kapena kuti, “sekeli yoyera.”
Gera imodzi inali yofanana ndi magalamu 0.57. Onani Zakumapeto B14.
Mʼchilankhulo choyambirira, “yakafungo kokhazika mtima pansi.”
Limeneli ndi pangano losatha komanso limene silingasinthidwe.
Mʼchilankhulo choyambirira, “nʼkusamba thupi lake.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “nʼkusamba thupi lake.”
Kapena kuti, “chimene chivundikiro chake sanachimange bwino ndi chingwe.”
Kutanthauza “Kukangana.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “masiku ambiri.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “dzanja lamphamvu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “anagona limodzi ndi makolo ake.”
Kutanthauza “Chinthu chimene chaperekedwa kuti chiwonongedwe.”
Kapena kuti, “njoka zamoto.”
Kapena kuti, “njoka yamoto.”
Kapena kuti, “mʼkhwawa la Zeredi.”
Kapena kuti, “makhwawa a Arinoni.”
Kapena kuti, “mʼmakhwawamo.”
Kapena kuti, “Imbani.”
Mabaibulo ena amati, “chipululu.”
Zikuoneka kuti umenewu ndi mtsinje wa Firate.
Mʼchilankhulo choyambirira, “pabulu wamkazi.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “anatsegula pakamwa pa bulu wamkaziyo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mawu okhawo amene Mulungu angaike mʼkamwa mwangamu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “anaika mawu mʼkamwa mwa Balamu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mawu amene Yehova waika mʼkamwa mwangamu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “nʼkumuika mawu awa mʼkamwa.”
Kapena kuti, “amene amadziimba mlandu.”
Mwina nyama imeneyi inali yooneka ngati njati.
Mabaibulo ena amati, “chipululu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ataona kuti ndi zabwino mʼmaso mwa Yehova.”
Kapena kuti, “makhwawa.”
Kapena kuti, “mbadwa.”
“Kukungudza” ndi kuchotseratu mnofu wonse pafupa tikamadya nyama.
Mʼchilankhulo choyambirira, “chochokera mumtima mwanga.”
Kutanthauza kuti anali oyamba kuukira Aisiraeli atatuluka mʼdziko la Iguputo.
“Kayini” akuimira fuko la “Akeni.”
Kapena kuti, “mkondo waungʼono.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “inatsegula pakamwa pake.”
Kapena kuti, “mogwirizana ndi chiwerengero cha mayina amene analembedwa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “udzagona limodzi ndi makolo ako.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Mulungu wa mizimu ya zamoyo zonse.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “munthu amene mwa iye muli mzimu.”
Kapena kuti, “ulemerero wako.”
Kapena kuti, “zimene Mulungu walamula,” mwina kudzera mwa Yoswa kapena Eleazara.
Mʼchilankhulo choyambirira, “kafungo kokhazika mtima pansi.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “pakati pa madzulo awiri.” Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa efa ndi lofanana ndi malita 2.2. Onani Zakumapeto B14.
Muyezo wa hini ndi wofanana ndi malita 3.67. Onani Zakumapeto B14.
Mʼchilankhulo choyambirira, “yakafungo kokhazika mtima pansi.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “pakati pa madzulo awiri.” Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mʼchilankhulo choyambirira, “yakafungo kokhazika mtima pansi.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “kwa miyezi yanu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “yakafungo kokhazika mtima pansi.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “yakafungo kokhazika mtima pansi.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “yakafungo kokhazika mtima pansi.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “yakafungo kokhazika mtima pansi.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “zakafungo kokhazika mtima pansi.”
Ankasonyeza chisoni chimenechi posala kudya ndiponso kudzimana zinthu zina.
Mʼchilankhulo choyambirira, “yakafungo kokhazika mtima pansi.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “yakafungo kokhazika mtima pansi.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “yakafungo kokhazika mtima pansi.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “udzagona limodzi ndi makolo ako.”
Kapena kuti, “kuti akhale mʼgulu la asilikali lokamenyana.”
Kapena kuti, “amene anali mʼgulu la asilikali.”
Kapena kuti, “misasa yawo yonse yokhala ndi mpanda.”
Sekeli imodzi inali yofanana ndi magalamu 11.4. Onani Zakumapeto B14.
Kapena kuti, “kukhwawa la Esikolo.”
Kapena kuti, “anamanganso.”
Kutanthauza “Midzi Ingʼonoingʼono ya Yairi.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mogwirizana ndi magulu awo ankhondo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ndi dzanja limene lakwezedwa.”
Zikuoneka kuti dzinali ndi chidule cha dzina lakuti Iye-abarimu.
Kapena kuti, “mafano achitsulo chosungunula.”
Imeneyi ndi Nyanja Yakufa.
Kapena kuti, “kukhwawa la Iguputo.”
Imeneyi ndi Nyanja Yaikulu ya Mediterranean.
Imeneyi ndi nyanja ya Mediterranean.
Kapena kuti, “polowera ku Hamati.”
Imeneyi ndi nyanja ya Genesareti, kapena kuti Nyanja ya Galileya.
Mʼchilankhulo choyambirira, “mikono 1000.” Onani Zakumapeto B14.
Mʼchilankhulo choyambirira, “pomubisalira.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “popanda kumubisalira.”