UTHENGA WABWINO WOLEMBEDWA NDI MATEYU
1 Buku la mzere wa makolo a Yesu Khristu,* mwana wa Davide,+ mwana wa Abulahamu:+
Isaki anabereka Yakobo.+
Yakobo anabereka Yuda+ ndi azichimwene ake.
3 Yuda anabereka Perezi ndi Zera,+ ndipo mayi awo anali Tamara.
Perezi anabereka Hezironi.+
Hezironi anabereka Ramu.+
4 Ramu anabereka Aminadabu.
Aminadabu anabereka Naasoni.+
Naasoni anabereka Salimoni.
5 Salimoni anabereka Boazi, ndipo mayi ake anali Rahabi.+
Boazi anabereka Obedi, ndipo mayi ake anali Rute.+
Obedi anabereka Jese.+
Davide anabereka Solomo,+ yemwe mayi ake anali mkazi wa Uriya.
7 Solomo anabereka Rehobowamu.+
Rehobowamu anabereka Abiya.
Abiya anabereka Asa.+
Yehosafati anabereka Yehoramu.+
Yehoramu anabereka Uziya.
Yotamu anabereka Ahazi.+
Ahazi anabereka Hezekiya.+
10 Hezekiya anabereka Manase.+
Manase anabereka Amoni.+
Amoni anabereka Yosiya.+
11 Yosiya+ anabereka Yekoniya+ ndi azichimwene ake pa nthawi imene Ayuda anatengedwa kupita ku Babulo.+
12 Ayuda atatengedwa kupita ku Babulo, Yekoniya anabereka Salatiyeli.
Salatiyeli anabereka Zerubabele.+
13 Zerubabele anabereka Abiyudi.
Abiyudi anabereka Eliyakimu.
Eliyakimu anabereka Azoro.
14 Azoro anabereka Zadoki.
Zadoki anabereka Akimu.
Akimu anabereka Eliyudi.
15 Eliyudi anabereka Eleazara.
Eleazara anabereka Matani.
Matani anabereka Yakobo.
16 Yakobo anabereka Yosefe mwamuna wake wa Mariya, amene anabereka Yesu,+ wotchedwa Khristu.+
17 Choncho mibadwo yonse kuchokera pa Abulahamu kukafika pa Davide inalipo mibadwo 14. Kuchokera pa Davide kukafika nthawi imene Ayuda anatengedwa kupita ku Babulo panali mibadwo 14. Kuchokera pa nthawi imene Ayudawo anatengedwa kupita ku Babulo kukafika pa Khristu, panali mibadwo 14.
18 Zimene zinachitika kuti Yesu Khristu abadwe ndi izi: Pa nthawi imene mayi ake Mariya anali atalonjezedwa ndi Yosefe kuti adzamukwatira, Mariyayo anapezeka kuti ndi woyembekezera mwa mzimu woyera*+ asanakwatirane. 19 Koma chifukwa chakuti mwamuna wake Yosefe anali munthu wolungama ndipo sanafune kumuchititsa manyazi kwa anthu, anaganiza zomusiya mwachinsinsi.*+ 20 Koma ataganizira mozama za nkhani imeneyi, mngelo wa Yehova* anamuonekera mʼmaloto nʼkumuuza kuti: “Yosefe, mwana wa Davide, usaope kutenga Mariya mkazi wako nʼkupita naye kunyumba, popeza iye ndi woyembekezera chifukwa cha mphamvu ya mzimu woyera.+ 21 Iye adzabereka mwana wamwamuna ndipo udzamupatse dzina lakuti Yesu,*+ chifukwa adzapulumutsa anthu ake ku machimo awo.”+ 22 Zonsezi zinachitikadi kuti zimene Yehova* ananena kudzera mwa mneneri wake zikwaniritsidwe. Iye anati: 23 “Tamverani! Namwali adzakhala woyembekezera ndipo adzabereka mwana wamwamuna. Mwanayo adzamʼpatsa dzina lakuti Emanueli,”+ limene akalimasulira limatanthauza kuti “Mulungu Ali Nafe.”+
24 Ndiyeno Yosefe anadzuka nʼkuchita mogwirizana ndi zimene mngelo wa Yehova* anamuuza. Anatenga mkazi wake nʼkupita naye kunyumba. 25 Koma sanagone naye mpaka anabereka mwana wamwamuna.+ Mwanayo anamupatsa dzina lakuti Yesu.+
2 Yesu atabadwa ku Betelehemu+ wa ku Yudeya, pa nthawi ya ulamuliro wa Mfumu Herode,*+ okhulupirira nyenyezi ochokera Kumʼmawa anabwera ku Yerusalemu. 2 Iwo ananena kuti: “Kodi mfumu ya Ayuda+ imene yabadwa posachedwapa ili kuti? Chifukwa pamene tinali Kumʼmawa, tinaona nyenyezi yake ndipo tabwera kudzamugwadira.” 3 Mfumu Herode komanso anthu onse a mu Yerusalemu atamva zimenezi, anavutika mumtima. 4 Choncho Herode anasonkhanitsa ansembe aakulu ndi alembi onse a anthu, ndipo anawafunsa za kumene Khristu* adzabadwire. 5 Iwo anamuyankha kuti: “Adzabadwira ku Betelehemu+ wa ku Yudeya, chifukwa mneneri analemba zimenezi kuti: 6 ‘Iwe Betelehemu wamʼdziko la Yuda, si iwe mzinda waungʼono kwambiri kwa olamulira a Yuda, chifukwa mwa iwe mudzatuluka wolamulira amene azidzaweta anthu anga, Aisiraeli.’”+
7 Kenako Herode anaitanitsa mwachinsinsi okhulupirira nyenyezi aja ndipo atawafunsa mosamala, anadziwa nthawi yeniyeni imene nyenyeziyo inaonekera. 8 Ndiyeno powatumiza ku Betelehemu, iye anawauza kuti: “Pitani mukamufunefune mwanayo mosamala. Mukakamupeza mubwere kudzandidziwitsa kuti nanenso ndipite kukamugwadira.” 9 Atamva zimene mfumu inanena, anapitiriza ulendo wawo. Kenako nyenyezi imene anaiona ali Kumʼmawa+ ija inawatsogolera mpaka inakaima pamwamba pa nyumba imene munali mwanayo. 10 Ataona kuti nyenyeziyo yaima, anasangalala kwambiri. 11 Atalowa mʼnyumbamo, anaona mwana uja ndi mayi ake Mariya ndipo anagwada nʼkumuweramira. Kenako anatulutsa chuma chawo nʼkupereka kwa mwanayo golide, lubani ndi mule monga mphatso. 12 Koma chifukwa chakuti Mulungu anawachenjeza kudzera mʼmaloto+ kuti asapitenso kwa Herode, iwo anabwerera kudziko lakwawo kudzera njira ina.
13 Okhulupirira nyenyezi aja atachoka, mngelo wa Yehova* anaonekera kwa Yosefe mʼmaloto+ nʼkumuuza kuti: “Nyamuka, tenga mwanayu ndi mayi ake ndipo uthawire ku Iguputo. Ukakhale kumeneko kufikira nthawi imene ndidzakuuze, chifukwa Herode akufuna kuyamba kufunafuna mwanayu kuti amuphe.” 14 Choncho Yosefe anadzuka usiku womwewo nʼkutenga mwana uja ndi mayi ake ndipo anachoka kumeneko nʼkupita ku Iguputo. 15 Iye anakhala kumeneko mpaka Herode atamwalira. Zimenezi zinakwaniritsa zimene Yehova* ananena kudzera mwa mneneri wake kuti: “Ndinaitana mwana wangayu kuti atuluke mu Iguputo.”+
16 Ndiyeno Herode ataona kuti okhulupirira nyenyezi aja amupusitsa, anakwiya koopsa. Choncho anatumiza anthu kukapha ana onse aamuna mʼBetelehemu ndi mʼzigawo zake zonse, kuyambira azaka ziwiri kutsika mʼmunsi. Anasankha kupha ana a zaka zimenezi mogwirizana ndi zimene okhulupirira nyenyezi aja anamuuza.+ 17 Zimenezi zinakwaniritsa mawu amene Mulungu ananena kudzera mwa mneneri Yeremiya kuti: 18 “Mawu anamveka ku Rama. Kunamveka kulira mofuula ndiponso momvetsa chisoni. Anali Rakele+ amene ankalirira ana ake ndipo sanamve kutonthozedwa, chifukwa ana akewo kunalibenso.”+
19 Herode atamwalira, mngelo wa Yehova* anaonekera mʼmaloto+ kwa Yosefe ku Iguputo 20 ndipo anamuuza kuti: “Nyamuka, tenga mwanayu ndi mayi ake ndipo upite mʼdziko la Isiraeli, chifukwa amene ankafuna kupha mwanayu* anamwalira.” 21 Choncho Yosefe ananyamuka nʼkutenga mwanayo ndi mayi ake nʼkukalowa mʼdziko la Isiraeli. 22 Koma atamva kuti Arikelao ndi amene akulamulira mʼmalo mwa bambo ake Herode ku Yudeya, anachita mantha kupita kumeneko. Komanso chifukwa chakuti Mulungu anamuchenjeza mʼmaloto,+ iye anapita mʼdera la Galileya.+ 23 Atafika kumeneko anakakhala mumzinda wotchedwa Nazareti+ kuti akwaniritse mawu amene Mulungu ananena kudzera mwa aneneri kuti: “Iye adzatchedwa Mnazareti.”*+
3 Mʼmasiku amenewo, Yohane+ Mʼbatizi anapita mʼchipululu cha Yudeya nʼkuyamba kulalikira.+ 2 Iye ankalalikira kuti: “Lapani, chifukwa Ufumu wakumwamba wayandikira.”+ 3 Mneneri Yesaya ananeneratu za iyeyu+ mʼmawu awa: “Winawake akufuula mʼchipululu kuti: ‘Konzani njira ya Yehova!* Muwongole misewu yake.’”+ 4 Yohane ankavala chovala chaubweya wa ngamila ndi lamba wachikopa mʼchiuno mwake.+ Chakudya chake chinali dzombe ndi uchi.+ 5 Choncho anthu ochokera ku Yerusalemu ndi mʼchigawo chonse cha Yudeya ndiponso ochokera mʼmidzi yonse yapafupi ndi Yorodano ankapita kwa iye.+ 6 Iye ankawabatiza* mumtsinje wa Yorodano+ ndipo anthuwo ankaulula machimo awo poyera.
7 Yohane ataona Afarisi ndi Asaduki+ ambiri akubwera ku ubatizowo, anawauza kuti: “Ana a njoka inu,+ ndi ndani wakuchenjezani kuti muthawe mkwiyo umene ukubwerawo?+ 8 Ndiyetu mubale zipatso zosonyeza kulapa. 9 Musamadzinamize kuti, ‘Tili ndi atate wathu Abulahamu.’+ Chifukwa ndikukuuzani kuti Mulungu akhoza kupangira Abulahamu ana kuchokera kumiyala iyi. 10 Nkhwangwa yaikidwa kale pamizu yamitengo. Choncho mtengo uliwonse wosabereka zipatso zabwino udulidwa nʼkuponyedwa pamoto.+ 11 Ine ndikukubatizani mʼmadzi chifukwa chakuti mwalapa,+ koma amene akubwera mʼmbuyo mwanga ndi wamphamvu kuposa ine, ndipo sindili woyenera kumuvula nsapato zake.*+ Ameneyo adzakubatizani ndi mzimu woyera+ komanso moto.+ 12 Fosholo yake youluzira mankhusu* ili mʼmanja mwake, ndipo malo ake opunthirapo mbewu adzawayeretseratu kuti mbee! Tirigu adzamututira munkhokwe, koma mankhusu adzawawotcha ndi moto+ umene sungazimitsidwe.”
13 Kenako Yesu anabwera kwa Yohane ku Yorodano kuchokera ku Galileya, kuti iye amubatize.+ 14 Koma Yohane anayesa kumuletsa ponena kuti: “Ineyo ndi amene ndikuyenera kubatizidwa ndi inu, ndiye nʼchifukwa chiyani mukubwera kwa ine?” 15 Yesu anamuyankha kuti: “Pa nthawi ino yokha lola kuti zikhale choncho, chifukwa tikufunikira kuchita zimenezi kuti tikwaniritse chilungamo chonse.” Atatero, anasiya kumuletsa. 16 Atabatizidwa, nthawi yomweyo Yesu anavuuka mʼmadzimo. Pamenepo kumwamba kunatseguka,+ ndipo Yohane anaona mzimu wa Mulungu ukutsika ngati nkhunda nʼkudzamutera.+ 17 Panamvekanso mawu ochokera kumwamba+ onena kuti: “Uyu ndi Mwana wanga+ wokondedwa ndipo amandisangalatsa kwambiri.”+
4 Kenako mzimu unatsogolera Yesu kuchipululu ndipo kumeneko anayesedwa+ ndi Mdyerekezi.+ 2 Atasala kudya masiku 40 masana ndi usiku, anamva njala. 3 Ndiyeno Woyesayo+ anabwera nʼkumuuza kuti: “Ngati ndinu mwana wa Mulungu, uzani miyalayi kuti isanduke mitanda ya mkate.” 4 Koma iye anayankha kuti, “Malemba amati: ‘Munthu sangakhale ndi moyo ndi chakudya chokha, koma ndi mawu alionse ochokera mʼkamwa mwa Yehova.’”*+
5 Kenako Mdyerekezi anamutenga nʼkupita naye mumzinda woyera,+ ndipo anamukweza pamwamba pa khoma la mpanda wa kachisi*+ 6 nʼkumuuza kuti: “Ngati ndinu mwana wa Mulungu mudziponye pansi, paja Malemba amati: ‘Iye adzalamula angelo ake zokhudza inu,’ komanso amati, ‘Adzakunyamulani mʼmanja mwawo, kuti phazi lanu lisawombe mwala.’”+ 7 Koma Yesu anamuyankha kuti: “Malemba amanenanso kuti: ‘Yehova* Mulungu wanu musamamuyese.’”+
8 Kenako Mdyerekezi anamutenganso nʼkupita naye paphiri lalitali kwambiri ndipo anamuonetsa maufumu onse apadziko ndi ulemerero wawo.+ 9 Ndiyeno anamuuza kuti: “Ndikupatsani zinthu zonsezi ngati mutagwada pansi kamodzi kokha nʼkundilambira.” 10 Koma Yesu anamuyankha kuti: “Choka Satana! Chifukwa Malemba amati, ‘Yehova* Mulungu wako ndi amene uyenera kumulambira+ ndipo uyenera kutumikira iye yekha basi.’”+ 11 Kenako Mdyerekezi uja anamusiya+ ndipo kunabwera angelo nʼkuyamba kumutumikira.+
12 Tsopano Yesu atamva kuti Yohane amutsekera mundende,+ anachoka kumeneko nʼkupita ku Galileya.+ 13 Kenako atachoka ku Nazareti, anafika ku Kaperenao+ nʼkupeza malo okhala mʼmbali mwa nyanja mʼzigawo za Zebuloni ndi Nafitali, 14 kuti mawu amene Mulungu ananena kudzera mwa mneneri Yesaya akwaniritsidwe. Iye ananena kuti: 15 “Anthu amene akukhala mʼdziko la Zebuloni ndi dziko la Nafitali, mʼmbali mwa msewu wakunyanja kutsidya lina la Yorodano, ku Galileya kumene kunkakhala anthu a mitundu ina, 16 anthu amene ankakhala mumdima anaona kuwala kwakukulu, ndipo anthu amene ankakhala mʼdera lamthunzi wa imfa, kuwala+ kunawaunikira.”+ 17 Kuyambira nthawi imeneyo, Yesu anayamba kulalikira kuti: “Lapani, chifukwa Ufumu wakumwamba wayandikira.”+
18 Pamene ankayenda mʼmbali mwa nyanja ya Galileya,* Yesu anaona amuna awiri apachibale akuponya ukonde wophera nsomba mʼnyanja. Iwo anali asodzi ndipo mayina awo anali Simoni wotchedwa Petulo+ ndi Andireya.+ 19 Iye anawauza kuti: “Nditsatireni ndipo ndikusandutsani asodzi a anthu.”+ 20 Nthawi yomweyo iwo anasiya maukonde awo nʼkumutsatira.+ 21 Atadutsa pamenepo, anaona amuna enanso awiri apachibale, Yakobo mwana wa Zebedayo ndi mchimwene wake Yohane.+ Iwo anali mʼngalawa limodzi ndi bambo awo, a Zebedayo, akusoka maukonde awo, ndipo anawaitana.+ 22 Nthawi yomweyo anasiya ngalawa ija ndi bambo awo nʼkumutsatira.
23 Atatero, anayendayenda mʼGalileya+ yense ndipo ankaphunzitsa mʼmasunagoge+ mwawo, ankalalikira uthenga wabwino wa Ufumu komanso ankachiritsa matenda amtundu uliwonse amene anthu ankadwala.+ 24 Choncho mbiri yake inafalikira mu Siriya monse. Anthu anamubweretsera onse amene ankadwala matenda osiyanasiyana komanso amene ankamva kupweteka mʼthupi,+ ogwidwa ndi ziwanda,+ akhunyu+ komanso anthu akufa ziwalo ndipo iye anawachiritsa. 25 Choncho anthu ambirimbiri ochokera ku Galileya, ku Dekapoli,* ku Yerusalemu, ku Yudeya komanso kutsidya lina la Yorodano, anamutsatira.
5 Yesu ataona gulu la anthu, anakwera mʼphiri ndipo atakhala pansi, ophunzira ake anabwera kwa iye. 2 Kenako anayamba kuwaphunzitsa kuti:
3 “Osangalala ndi anthu amene amazindikira zosowa zawo zauzimu+ chifukwa Ufumu wakumwamba ndi wawo.
4 Osangalala ndi anthu amene akumva chisoni chifukwa adzalimbikitsidwa.+
5 Osangalala ndi anthu ofatsa+ chifukwa adzalandira dziko lapansi.+
6 Osangalala ndi anthu amene akumva njala ndi ludzu+ la chilungamo chifukwa adzakhuta.+
7 Osangalala ndi anthu achifundo+ chifukwa adzachitiridwa chifundo.
8 Osangalala ndi anthu oyera mtima+ chifukwa adzaona Mulungu.
9 Osangalala ndi anthu amene amabweretsa mtendere+ chifukwa adzatchedwa ana a Mulungu.
10 Osangalala ndi anthu amene azunzidwa chifukwa cha chilungamo+ chifukwa Ufumu wakumwamba ndi wawo.
11 Ndinu osangalala pamene anthu akukunyozani,+ kukuzunzani komanso kukunamizirani+ zoipa zilizonse chifukwa cha ine.+ 12 Sangalalani ndi kukondwera+ kwambiri chifukwa mphoto+ imene Mulungu adzakupatseni ndi yaikulu,* ndipo umu ndi mmenenso anazunzira aneneri amene analipo inu musanakhaleko.+
13 Inu ndinu mchere+ wa dziko lapansi. Koma ngati mchere watha mphamvu, kodi mphamvu yakeyo angaibwezeretse bwanji? Sungagwirenso ntchito iliyonse koma ungafunike kungoutaya kunja+ kuti anthu azikaupondaponda.
14 Inu ndinu kuwala kwa dziko.+ Mzinda ukakhala paphiri subisika. 15 Anthu akayatsa nyale saivindikira ndi dengu, koma amaiika pachoikapo nyale ndipo imaunikira onse mʼnyumbamo.+ 16 Mofanana ndi zimenezi, nanunso muzionetsa kuwala kwanu pamaso pa anthu,+ kuti aone ntchito zanu zabwino+ nʼkulemekeza Atate wanu wakumwamba.+
17 Musaganize kuti ndinabwera kudzawononga Chilamulo kapena zimene aneneri analemba. Sindinabwere kudzaziwononga koma kudzazikwaniritsa.+ 18 Ndithu ndikukuuzani kuti kumwamba ndi dziko lapansi zingachoke mosavuta, kusiyana nʼkuti chilembo chimodzi chachingʼono kwambiri kapena kachigawo kakangʼono ka chilembo cha mʼChilamulo kachoke zinthu zonse zisanachitike.+ 19 Choncho aliyense amene waphwanya lililonse la malamulo aangʼono awa nʼkumaphunzitsanso ena kuchita zomwezo, adzakhala wosayenera kulowa mu Ufumu wakumwamba. Koma aliyense wotsatira ndi kuphunzitsa malamulowa adzakhala woyenera kulowa mu Ufumu wakumwamba. 20 Ndikukuuzani kuti ngati chilungamo chanu sichimaposa cha alembi ndi Afarisi,+ ndithu simudzalowa mu Ufumu wakumwamba.+
21 Inu munamva kuti anthu akale anauzidwa kuti: ‘Musaphe munthu.+ Aliyense amene wapha munthu wapalamula mlandu wa kukhoti.’+ 22 Koma ine ndikukuuzani kuti aliyense wopitiriza kupsera mtima+ mʼbale wake wapalamula mlandu wa kukhoti. Ndipo aliyense wonenera mʼbale wake mawu achipongwe wapalamula mlandu wa ku Khoti Lalikulu. Komanso aliyense wonena mnzake kuti, ‘Ndiwe chitsiru!’ adzapita ku Gehena* wamoto.+
23 Ndiye ngati wabweretsa mphatso yako paguwa lansembe,+ ndipo uli pomwepo wakumbukira kuti mʼbale wako ali nawe chifukwa, 24 siya mphatso yako patsogolo pa guwa lansembe pomwepo nʼkuchokapo. Choyamba pita ukakhazikitse mtendere ndi mʼbale wakoyo. Kenako ukabwerenso nʼkudzapereka mphatso yakoyo.+
25 Uzithetsa nkhani mofulumira ndi munthu wokuimba mlandu pamene ukupita naye kukhoti, kuti mwina wokuimba mlanduyo asakakupereke kwa woweruza. Komanso kuti woweruzayo asakakupereke kwa msilikali wakukhoti kuti akuponye mʼndende.+ 26 Kunena zoona, sudzatulukamo mpaka utalipira kakhobidi kotsirizira kochepa mphamvu kwambiri.*
27 Inu munamva kuti anati: ‘Musachite chigololo.’+ 28 Koma ine ndikukuuzani kuti aliyense woyangʼanitsitsa mkazi+ mpaka kumulakalaka, wachita naye kale chigololo mumtima mwake.+ 29 Ndiye ngati diso lako lakumanja limakuchimwitsa,* ulikolowole nʼkulitaya.+ Chifukwa ndi bwino kuti ukhale wopanda chiwalo chimodzi kusiyana ndi kuti thupi lako lonse lidzaponyedwe mʼGehena.*+ 30 Komanso ngati dzanja lako lamanja limakuchimwitsa, ulidule nʼkulitaya.+ Chifukwa ndi bwino kuti ukhale wopanda chiwalo chimodzi kusiyana ndi kuti thupi lako lonse lidzaponyedwe mʼGehena.*+
31 Pajanso anati: ‘Aliyense amene akuthetsa ukwati ndi mkazi wake, azipatsa mkaziyo kalata yothetsera ukwati.’+ 32 Koma ine ndikukuuzani kuti aliyense amene wathetsa ukwati ndi mkazi wake, osati chifukwa cha chiwerewere,* amachititsa kuti mkaziyo achite chigololo akakwatiwanso. Ndipo aliyense amene wakwatira mkazi wosiyidwayo nayenso wachita chigololo.+
33 Komanso munamva kuti anthu akale anauzidwa kuti: ‘Musamalumbire koma osachita,+ mʼmalomwake muzikwaniritsa zimene mwalonjeza kwa Yehova.’*+ 34 Koma ine ndikukuuzani kuti: Musamalumbire nʼkomwe,+ kutchula kumwamba, chifukwa nʼkumene kuli mpando wachifumu wa Mulungu, 35 kapena kutchula dziko lapansi chifukwa ndi chopondapo mapazi ake,+ kapenanso kutchula Yerusalemu chifukwa ndi mzinda wa Mfumu yamphamvu.+ 36 Musamalumbire potchula mutu wanu, chifukwa simungathe kusandutsa tsitsi lanu, ngakhale limodzi, kuti likhale loyera kapena lakuda. 37 Tangotsimikizani kuti mukati ‘Indeʼ akhaledi inde, ndipo mukati ‘Ayiʼ akhaledi ayi,+ chifukwa mawu owonjezera pamenepa ndi ochokera kwa woipayo.+
38 Inu munamva kuti anati: ‘Diso kulipira diso, ndi dzino kulipira dzino.’+ 39 Koma ine ndikukuuzani kuti: Musamalimbane ndi munthu woipa, koma wina akakumenyani mbama patsaya lakumanja, muzimupatsanso tsaya linalo.+ 40 Ngati munthu akufuna kukutengera kukhoti kuti akulande malaya ako amkati, uzimupatsanso akunja.+ 41 Ngati munthu waudindo wakulamula kuti umunyamulire katundu mtunda wa kilomita imodzi,* uzimunyamulira mtunda wa makilomita awiri. 42 Munthu akakupempha kanthu uzimupatsa ndipo munthu amene akufuna kukongola* kanthu kwa iwe usamukanize.+
43 Inu munamva kuti anati: ‘Uzikonda mnzako+ ndipo uzidana ndi mdani wako.’ 44 Koma ine ndikukuuzani kuti: Pitirizani kukonda adani anu+ ndi kupempherera amene akukuzunzani,+ 45 kuti musonyeze kuti ndinudi ana a Atate wanu wakumwamba.+ Chifukwa iye amawalitsira dzuwa lake anthu abwino ndi oipa omwe, ndipo amagwetsera mvula anthu olungama ndi osalungama omwe.+ 46 Ndiye mukamakonda anthu okhawo amene amakukondani, mudzalandira mphoto yotani?+ Kodi okhometsa msonkho sachitanso zomwezo? 47 Ngati mukupereka moni kwa abale anu okha, kodi nʼchiyani chachilendo chimene mukuchita? Kodi anthu a mitundu ina nawonso sachita zomwezo? 48 Choncho khalani angwiro,* mofanana ndi Atate wanu wakumwamba amene ndi wangwiro.”+
6 “Samalani kuti musamachite zinthu zachilungamo pamaso pa anthu nʼcholinga choti akuoneni.+ Mukamachita zimenezi simudzalandira mphoto kwa Atate wanu amene ali kumwamba. 2 Choncho mukamapereka mphatso zachifundo,* musamalize lipenga ngati mmene amachitira anthu achinyengo mʼmasunagoge ndi mʼmisewu nʼcholinga choti anthu awatamande. Ndithu ndikukuuzani, anthu amenewo akulandiriratu mphoto yawo yonse. 3 Koma iwe ukamapereka mphatso zachifundo, dzanja lako lamanzere lisadziwe zimene dzanja lako lamanja likuchita, 4 kuti mphatso zako zachifundo zikhale zachinsinsi. Ukatero Atate wako amene akuona zimene zikuchitika ngakhale kuti iweyo sungathe kuwaona, adzakubwezera.+
5 Komanso mukamapemphera, musamachite zimene anthu achinyengo amachita.+ Chifukwa iwo amakonda kuima mʼmasunagoge ndi mumphambano za misewu ikuluikulu kuti anthu aziwaona.+ Ndithu ndikukuuzani, anthu amenewo akulandiriratu mphoto yawo yonse. 6 Koma iwe ukamapemphera, uzilowa mʼchipinda chako nʼkutseka chitseko ndipo uzipemphera kwa Atate wako amene sungathe kuwaona.+ Ukatero Atate wako amene akuona zimene zikuchitika ngakhale kuti iweyo sungathe kuwaona, adzakubwezera. 7 Ukamapemphera, usamanene mawu omweomwewo mobwerezabwereza ngati mmene anthu a mitundu ina amachitira. Iwo amaganiza kuti Mulungu awamvetsera akanena mawu ambirimbiri. 8 Choncho inu musakhale ngati iwowo, chifukwa Atate wanu amadziwa zimene mukufunikira+ musanamupemphe nʼkomwe.
9 Koma inu muzipemphera chonchi:+
‘Atate wathu wakumwamba, dzina lanu+ liyeretsedwe.*+ 10 Ufumu wanu ubwere.+ Zofuna zanu+ zichitike padziko lapansi pano ngati mmene zilili kumwamba.+ 11 Mutipatse chakudya chimene* tikufunikira lero.+ 12 Mutikhululukire zolakwa* zathu chifukwa ifenso takhululukira amene atilakwira.*+ 13 Tithandizeni kuti tisagonje tikamayesedwa,*+ koma mutiteteze kwa woipayo.’+
14 Mukamakhululukira anthu machimo awo, inunso Atate wanu wakumwamba adzakukhululukirani.+ 15 Koma ngati simukhululukira anthu machimo awo, Atate wanu sadzakukhululukiraninso machimo anu.+
16 Mukamasala kudya,+ siyani kuonetsa nkhope yachisoni ngati mmene anthu achinyengo aja amachitira. Iwo sasamalira nkhope* zawo kuti anthu ena adziwe kuti akusala kudya.+ Ndithu ndikukuuzani, anthu amenewo akulandiriratu mphoto yawo yonse. 17 Koma iwe ukamasala kudya, uzisukusula nkhope yako komanso kupaka mafuta mʼmutu mwako, 18 kuti anthu ena asadziwe kuti ukusala kudya, koma Atate wako wokha amene sungathe kuwaona. Ukatero Atate wako amene akuona zimene zikuchitika ngakhale kuti iweyo sungathe kuwaona, adzakubwezera.
19 Siyani kudziunjikira chuma padziko lapansi,+ pomwe njenjete* komanso dzimbiri zimawononga ndiponso pomwe akuba amathyola nʼkuba. 20 Koma unjikani chuma chanu kumwamba,+ kumene njenjete kapena dzimbiri sizingawononge+ ndiponso kumene akuba sangathyole nʼkuba. 21 Chifukwa kumene kuli chuma chako, mtima wako udzakhalanso komweko.
22 Nyale ya thupi ndi diso.+ Choncho ngati diso lako likuyangʼana* pachinthu chimodzi, thupi lako lonse lidzakhala lowala kwambiri. 23 Koma ngati diso lako lili ladyera,*+ thupi lako lonse lidzachita mdima. Choncho ngati kuwala kumene kuli mwa iwe ndi mdima, ndiye kuti mdimawo ndi wandiweyani!
24 Kapolo sangatumikire ambuye awiri, chifukwa akhoza kudana ndi mmodzi nʼkukonda winayo,+ kapena angakhale wokhulupirika kwa mmodzi nʼkunyoza winayo. Simungathe kutumikira Mulungu ndi Chuma nthawi imodzi.+
25 Pa chifukwa chimenechi, ndikukuuzani kuti: Siyani kudera nkhawa za moyo wanu,+ kuti mudzadya chiyani kapena kuti mudzamwa chiyani kapenanso kudera nkhawa za matupi anu kuti mudzavala chiyani.+ Kodi moyo si wofunika kwambiri kuposa chakudya ndipo kodi thupi si lofunika kwambiri kuposa chovala?+ 26 Yangʼanitsitsani mbalame zamumlengalenga,+ pajatu sizifesa mbewu kapena kukolola kapenanso kusunga chakudya mʼnyumba zosungiramo zinthu. Koma Atate wanu wakumwamba amazidyetsa. Kodi inu si amtengo wapatali kuposa mbalame? 27 Ndi ndani wa inu amene angatalikitse moyo wake pangʼono pokha* chifukwa cha kuda nkhawa?+ 28 Komanso nʼchifukwa chiyani mukudera nkhawa nkhani ya zovala? Phunzirani mmene maluwa akutchire amakulira. Sagwira ntchito ndiponso sawomba nsalu. 29 Komatu ndikukuuzani kuti ngakhale Solomo+ mu ulemerero wake wonse sanavalepo zokongola ngati lililonse la maluwa amenewa. 30 Ndiye ngati Mulungu amaveka chonchi zomera zakutchire, zimene zimangokhalapo lero lokha mawa nʼkuzisonkheza pamoto, kodi iye sadzakuvekani kuposa pamenepo achikhulupiriro chochepa inu? 31 Choncho musamade nkhawa+ nʼkumanena kuti, ‘Tidya chiyani?’ kapena, ‘Timwa chiyani?’ kapenanso, ‘Tivala chiyani?’+ 32 Chifukwa anthu a mitundu ina akufunafuna mwakhama zinthu zonsezi. Koma Atate wanu wakumwamba akudziwa kuti inuyo mumafunikira zinthu zonsezi.
33 Choncho nthawi zonse muziika Ufumu ndi mfundo zolungama za Mulungu pamalo oyamba pa moyo wanu, ndipo iye adzakupatsani zinthu zina zonsezi.+ 34 Musamadere nkhawa za mawa,+ chifukwa mawalo lidzakhala ndi zodetsa nkhawa zakenso. Mavuto a tsiku lililonse ndi okwanira pa tsikulo.”
7 “Siyani kuweruza ena+ kuti inunso musaweruzidwe, 2 chifukwa mmene mumaweruzira ena inunso adzakuweruzani choncho.+ Ndipo muyezo umene mukuyezera ena iwonso adzakuyezerani womwewo.+ 3 Nanga nʼchifukwa chiyani umayangʼana kachitsotso mʼdiso la mʼbale wako, koma osaona mtanda wa denga la nyumba umene uli mʼdiso lako?+ 4 Kapena ungauze bwanji mʼbale wako kuti, ‘Taima ndikuchotse kachitsotso mʼdiso lako,’ pamene iwe mʼdiso lako muli mtanda wa denga la nyumba? 5 Wachinyengo iwe! Yamba wachotsa mtanda wa denga la nyumba umene uli mʼdiso lakowo. Ukatero udzatha kuona bwino moti udzakwanitsa kuchotsa kachitsotso mʼdiso la mʼbale wako.
6 Musamapatse agalu zinthu zopatulika, kapena kuponyera nkhumba ngale zanu,+ kuopera kuti zingapondeponde ngalezo kenako zingatembenuke nʼkukukhadzulani.
7 Pitirizani kupempha ndipo adzakupatsani.+ Pitirizani kufunafuna ndipo mudzapeza. Pitirizani kugogoda ndipo adzakutsegulirani.+ 8 Chifukwa aliyense wopempha amalandira,+ aliyense wofunafuna amapeza, ndipo aliyense wogogoda adzamutsegulira. 9 Inde, ndi ndani wa inu amene mwana wake atamupempha mkate angamupatse mwala? 10 Kapena atamupempha nsomba, kodi angamupatse njoka? 11 Choncho ngati inuyo mumadziwa kupereka mphatso zabwino kwa ana anu, ngakhale kuti ndinu oipa, kuli bwanji Atate wanu wakumwamba? Ndithudi, iye adzapereka mowolowa manja zinthu zabwino+ kwa amene akumupempha.+
12 Choncho zinthu zonse zimene mukufuna kuti anthu akuchitireni, inunso muwachitire zomwezo.+ Zimenezi ndi zomwe Chilamulo chimafuna komanso zimene aneneri analemba.+
13 Lowani pageti lalingʼono.+ Chifukwa msewu umene ukupita kuchiwonongeko ndi wotakasuka komanso geti lake ndi lalikulu ndipo anthu ambiri akudzera pageti limenelo. 14 Koma geti lolowera ku moyo ndi lalingʼono komanso msewu wake ndi wopanikiza ndipo amene akuupeza ndi ochepa.+
15 Chenjerani ndi aneneri abodza+ amene amabwera kwa inu atavala ngati nkhosa,+ koma mkati mwa mitima yawo ali ngati mimbulu yolusa.+ 16 Mudzawazindikira chifukwa cha zipatso zawo. Anthu sathyola mphesa paminga kapena nkhuyu pamtengo wa nthula, amatero kodi?+ 17 Mofanana ndi zimenezi, mtengo uliwonse wabwino umabereka zipatso zabwino, koma mtengo uliwonse wovunda umabereka zipatso zopanda pake.+ 18 Mtengo wabwino sungabereke zipatso zopanda pake ndipo mtengo wovunda sungabereke zipatso zabwino.+ 19 Mtengo uliwonse umene subereka zipatso zabwino amaudula nʼkuuponya pamoto.+ 20 Choncho anthu amenewo mudzawazindikira chifukwa cha zipatso zawo.+
21 Sikuti aliyense amene amanditchula kuti, ‘Ambuye, Ambuye,’ adzalowa Ufumu wakumwamba, koma yekhayo amene akuchita zimene Atate wanga wakumwamba amafuna.+ 22 Pa tsiku limenelo ambiri adzandiuza kuti: ‘Ambuye, Ambuye,+ kodi ife sitinalosere mʼdzina lanu ndi kutulutsa ziwanda mʼdzina lanu ndiponso kuchita ntchito zambiri zamphamvu mʼdzina lanu?’+ 23 Koma ine ndidzawauza kuti: ‘Sindikukudziwani ngakhale pangʼono! Chokani pamaso panga, anthu osamvera malamulo inu.’+
24 Choncho aliyense amene wamva mawu angawa nʼkuchita zimene wamvazo, adzafanana ndi munthu wanzeru, amene anamanga nyumba yake pathanthwe.+ 25 Ndiyeno kunagwa chimvula champhamvu ndipo madzi anasefukira. Kenako chimphepo chinawomba mwamphamvu, koma nyumbayo sinagwe chifukwa chakuti inakhazikika pathanthwepo. 26 Aliyense amene wamva mawu angawa koma osachita zimene wamvazo adzafanana ndi munthu wopusa amene anamanga nyumba yake pamchenga.+ 27 Ndiye kunagwa chimvula champhamvu ndipo madzi anasefukira. Kenako chimphepo chinawomba mwamphamvu moti nyumbayo inagwa+ ndipo kugwa kwake kunali kwakukulu.”
28 Yesu atamaliza kulankhula mawu amenewa, gulu la anthulo linakhudzidwa moti linadabwa ndi kaphunzitsidwe kake,+ 29 chifukwa ankawaphunzitsa monga munthu waulamuliro,+ osati ngati alembi awo.
8 Atatsika mʼphirimo, chigulu cha anthu chinamutsatira. 2 Kenako panafika munthu wakhate. Munthuyo anamugwadira nʼkunena kuti: “Ambuye, ndikudziwa kuti ngati mukufuna, mukhoza kundiyeretsa.”+ 3 Choncho Yesu anatambasula dzanja lake nʼkumukhudza ndipo ananena kuti: “Inde ndikufuna. Khala woyera.”+ Nthawi yomweyo khate lakelo linatha.+ 4 Ndiyeno Yesu anamuuza kuti: “Samala, usauze aliyense zimenezi,+ koma upite ukadzionetse kwa wansembe+ ndipo ukapereke mphatso imene Mose analamula,+ kuti ikhale umboni kwa iwo.”
5 Atalowa mumzinda wa Kaperenao, mtsogoleri wa asilikali anabwera kwa iye nʼkumupempha+ 6 kuti: “Ambuye, wantchito wanga wafa ziwalo moti ali chigonere mʼnyumba ndipo akuvutika koopsa.” 7 Iye anamuuza kuti: “Ndikafika kumeneko ndikamuchiritsa.” 8 Mtsogoleri wa asilikali uja anayankha kuti: “Ambuye, sindine munthu woyenera kuti inu mukalowe mʼnyumba mwanga, koma mungonena mawu okha ndipo wantchito wangayo achira. 9 Chifukwa inenso ndili ndi akuluakulu ondiyangʼanira komanso ndili ndi asilikali amene ndimawayangʼanira. Ndikauza mmodzi kuti, ‘Pita!’ amapita, wina ndikamuuza kuti, ‘Bwera!’ amabwera. Kapolo wanga ndikamuuza kuti, ‘Chita ichi!’ amachita.” 10 Yesu atamva zimenezo, anadabwa ndipo anauza amene ankamutsatira aja kuti: “Kunena zoona, mu Isiraeli sindinapezemo aliyense wachikhulupiriro chachikulu ngati chimenechi.+ 11 Koma ndikukuuzani kuti ambiri ochokera kumʼmawa ndi kumadzulo adzabwera nʼkukhala patebulo limodzi ndi Abulahamu, Isaki ndi Yakobo mu Ufumu wakumwamba,+ 12 pamene ana a Ufumuwo adzaponyedwa kunja kumdima. Kumeneko adzalira ndi kukukuta mano.”+ 13 Kenako Yesu anauza mtsogoleri wa asilikaliyo kuti: “Pita. Chifukwa chakuti wasonyeza chikhulupiriro, zimene wapemphazo zichitike.”+ Mu ola lomwelo wantchito uja anachira.+
14 Tsopano Yesu, atalowa mʼnyumba mwa Petulo, anaona apongozi aakazi a Petulo+ ali chigonere, akudwala malungo.*+ 15 Choncho anagwira dzanja la mayiwo+ ndipo malungowo anatheratu, moti anadzuka nʼkuyamba kumutumikira. 16 Koma chakumadzulo, anthu anamubweretsera anthu ambiri ogwidwa ndi ziwanda. Iye anatulutsa mizimu imeneyo ndi mawu okha ndipo anachiritsa anthu onse amene ankadwala. 17 Anachita zimenezi kuti zimene Mulungu ananena kudzera mwa mneneri Yesaya zikwaniritsidwe. Iye ananena kuti: “Iye anatenga matenda athu nʼkunyamula zowawa zathu.”+
18 Yesu ataona kuti gulu la anthu lamuzungulira, analamula kuti achoke nʼkupita kutsidya lina.+ 19 Ndiyeno kunabwera mlembi nʼkumuuza kuti: “Mphunzitsi, ndikutsatirani kulikonse kumene mungapite.”+ 20 Koma Yesu anamuuza kuti: “Nkhandwe zili ndi mapanga ndipo mbalame zamumlengalenga zili ndi zisa, koma Mwana wa munthu alibiretu poti nʼkutsamiritsa mutu wake.”+ 21 Kenako mmodzi mwa ophunzira ake anamuuza kuti: “Ambuye, ndiloleni ndiyambe ndapita kukaika maliro a bambo anga.”+ 22 Koma Yesu anamuyankha kuti: “Iwe upitirizebe kunditsatira, ndipo asiye akufa aike akufa awo.”+
23 Ndiyeno atakwera mʼngalawa, ophunzira ake anamʼtsatira.+ 24 Kenako panyanjapo panabuka mphepo yamphamvu moti mafunde ankalowetsa madzi mʼngalawamo, koma iye anali mʼtulo.+ 25 Ndipo iwo anapita kukamudzutsa kuti: “Ambuye, tipulumutseni tikufa!” 26 Koma iye anawafunsa kuti: “Nʼchifukwa chiyani mukuchita mantha chonchi, anthu achikhulupiriro chochepa inu?”+ Kenako anadzuka nʼkudzudzula mphepo ndi nyanjayo, ndipo panachita bata lalikulu.+ 27 Choncho amunawo anadabwa nʼkunena kuti: “Kodi munthu ameneyu ndi wotani? Ngakhale mphepo ndi nyanja zikumumvera.”
28 Atafika kutsidya linalo, mʼdera la Agadara, anakumana ndi amuna awiri ogwidwa ndi ziwanda akuchokera mʼmanda.*+ Amunawa anali ochititsa mantha kwambiri moti panalibe aliyense amene ankalimba mtima kudutsa msewu umenewo. 29 Nthawi yomweyo iwo anafuula kuti: “Kodi mukufuna chiyani kwa ife, Mwana wa Mulungu?+ Kodi mwabwera kudzatipatsa chilango+ nthawi yoikidwiratu isanakwane?”+ 30 Koma pamtunda wautali ndithu kuchokera pamenepo, panali nkhumba zambiri zimene zinkadya.+ 31 Choncho ziwandazo zinayamba kumʼchonderera kuti: “Ngati mukufuna kutitulutsa, mutitumize munkhumbazo.”+ 32 Iye anaziuza kuti: “Pitani!” Choncho zinatuluka nʼkukalowa munkhumba zija. Nthawi yomweyo nkhumba zonsezo zinathamangira kuphedi nʼkulumphira mʼnyanja, ndipo zinafera mʼmadzimo. 33 Koma abusa a ziwetozo anathawa ndipo atalowa mumzinda anafotokoza zonse, kuphatikizapo zimene zinachitikira amuna ogwidwa ndi ziwanda aja. 34 Zitatero, anthu onse mumzindawo anapita kukakumana ndi Yesu. Atamuona, anamʼpempha kuti achoke mʼdera lawolo.+
9 Choncho Yesu anakwera ngalawa nʼkuwolokera tsidya lina, ndipo anapita kumzinda umene ankakhala.+ 2 Kumeneko anthu anamubweretsera munthu wakufa ziwalo, atagona pamachira. Yesu ataona chikhulupiriro chawo, anauza wakufa ziwaloyo kuti: “Limba mtima mwanawe! Machimo ako akhululukidwa.”+ 3 Atatero, alembi ena ankanena chamumtima kuti: “Munthu ameneyu akunyoza Mulungu.” 4 Koma Yesu anadziwa zimene iwo ankaganiza ndipo anawafunsa kuti: “Nʼchifukwa chiyani mukuganiza zinthu zoipa mʼmitima mwanu?+ 5 Mwachitsanzo, chosavuta nʼchiti, kunena kuti, ‘Machimo ako akhululukidwa,’ kapena kunena kuti, ‘Nyamuka uyendeʼ?+ 6 Dikirani ndikuonetseni kuti Mwana wa munthu ali ndi mphamvu padziko lapansi zokhululukira machimo.” Kenako iye anauza wakufa ziwalo uja kuti: “Nyamuka, tenga machira akowa ndipo uzipita kwanu.”+ 7 Ndipo ananyamuka nʼkupita kwawo. 8 Gulu la anthulo litaona zimenezi, linagwidwa ndi mantha ndipo linatamanda Mulungu, amene anapereka mphamvu zimenezo kwa anthu.
9 Atachoka pamenepo, Yesu anaona munthu wina dzina lake Mateyu atakhala mu ofesi yokhomeramo msonkho, ndipo anamuuza kuti: “Ukhale wotsatira wanga.” Nthawi yomweyo ananyamuka nʼkumutsatira.+ 10 Nthawi inayake, pamene ankadya chakudya* mʼnyumba ina, kunabwera anthu ambiri okhometsa msonkho komanso ochimwa ndipo anayamba kudya* limodzi ndi Yesu ndi ophunzira ake.+ 11 Koma Afarisi ataona zimenezi anafunsa ophunzira ake kuti: “Nʼchifukwa chiyani mphunzitsi wanu amadya limodzi ndi anthu okhometsa msonkho komanso ochimwa?”+ 12 Iye atamva zimenezo, anayankha kuti: “Anthu abwinobwino safunikira dokotala, koma odwala ndi amene amamufuna.+ 13 Choncho pitani mukaphunzire tanthauzo la mawu akuti: ‘Ndikufuna chifundo, osati nsembe.’+ Chifukwa ine sindinabwere kudzaitana anthu olungama, koma ochimwa.”
14 Kenako ophunzira a Yohane anabwera kwa iye nʼkumufunsa kuti: “Nʼchifukwa chiyani ife ndi Afarisi timasala kudya koma ophunzira anu sasala kudya?”+ 15 Yesu anawayankha kuti: “Anzake a mkwati samva chisoni ngati mkwatiyo+ ali nawo limodzi, si choncho kodi? Koma masiku akubwera pamene mkwatiyo adzachotsedwa pakati pawo+ ndipo pa nthawiyo adzasala kudya. 16 Palibe amene amasokerera chigamba cha nsalu yatsopano pamalaya akunja akale. Chifukwa chigambacho chingakoke nʼkungʼamba malayawo ndipo kungʼambikako kungawonjezeke kwambiri.+ 17 Ndiponso anthu sathira vinyo watsopano mʼmatumba achikopa akale. Akachita zimenezo, matumba achikopawo amaphulika ndipo vinyoyo amatayika moti matumbawo amawonongeka. Koma anthu amathira vinyo watsopano mʼmatumba achikopa atsopano, ndipo zonse ziwiri zimasungika bwino.”
18 Pamene ankawauza zimenezi, wolamulira wina anamuyandikira. Kenako anamugwadira nʼkunena kuti: “Panopa mwana wanga wamkazi ayenera kuti wamwalira kale. Koma tiyeni mukamukhudze ndi dzanja lanu ndipo akhala ndi moyo.”+
19 Kenako Yesu ananyamuka ndi ophunzira ake nʼkumutsatira. 20 Ndiyeno mayi wina amene ankadwala matenda otaya magazi kwa zaka 12+ anafika kumbuyo kwake nʼkugwira ulusi wopota wamʼmphepete mwa malaya ake akunja,+ 21 chifukwa mumtima mwake ankanena kuti: “Ndikangogwira malaya ake akunja okhawo, ndichira ndithu.” 22 Yesu anatembenuka ndipo anaona mayiyo nʼkunena kuti: “Mwanawe, limba mtima, chikhulupiriro chako chakuchiritsa.”+ Kuchokera pa ola limenelo mayiyo anachira.+
23 Ndiyeno atalowa mʼnyumba ya wolamulira uja, anaona anthu akuliza zitoliro komanso gulu la anthu likulira mofuula.+ 24 Yesu anawauza kuti: “Tulukani muno, chifukwa mtsikanayu sanamwalire, koma akugona.”+ Atanena zimenezi, anthuwo anayamba kumuseka monyoza. 25 Anthu aja atawatulutsa panja, Yesu analowa nʼkugwira dzanja la mtsikanayo,+ ndipo iye anadzuka.+ 26 Nkhani imeneyi inamveka mʼdera lonselo.
27 Yesu akuchokera kumeneko, amuna awiri amene anali ndi vuto losaona+ anamutsatira akufuula kuti: “Mutichitire chifundo, Mwana wa Davide.” 28 Yesu atalowa mʼnyumba, amuna amene anali ndi vuto losaona aja anabwera kwa iye, ndipo anawafunsa kuti: “Kodi mukukhulupirira kuti ndingachite zimenezi?”+ Iwo anamuyankha kuti: “Inde, Ambuye.” 29 Kenako anawagwira mʼmaso+ nʼkunena kuti: “Mogwirizana ndi chikhulupiriro chanu zimene mukufunazo zichitike kwa inu.” 30 Maso awo anatseguka ndipo Yesu anawachenjeza mwamphamvu kuti: “Samalani, aliyense asadziwe zimenezi.”+ 31 Koma iwo atatuluka kunja, anafalitsa paliponse zokhudza iye mʼdera lonselo.
32 Pamene amuna awiriwo ankanyamuka, anthu anamubweretsera munthu wosalankhula amene anagwidwa ndi chiwanda.+ 33 Atatulutsa chiwandacho, munthu wosalankhulayo analankhula,+ moti gulu la anthulo linadabwa ndipo linanena kuti: “Zoterezi sizinaonekepo nʼkale lonse mu Isiraeli.”+ 34 Koma Afarisi ankanena kuti: “Ameneyu amatulutsa ziwanda ndi mphamvu ya wolamulira ziwanda.”+
35 Ndiyeno Yesu anayamba ulendo woyendera mizinda ndi midzi yonse. Iye ankaphunzitsa mʼmasunagoge awo komanso kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu ndipo ankachiritsa matenda amtundu uliwonse amene anthu ankadwala.+ 36 Ataona chigulu cha anthu, iye anawamvera chisoni,+ chifukwa anali onyukanyuka komanso opanda wowasamalira ngati nkhosa zimene zilibe mʼbusa.+ 37 Kenako anauza ophunzira ake kuti: “Inde, pali zinthu zambiri zofunika kukolola, koma antchito ndi ochepa.+ 38 Choncho pemphani Mwiniwake wa munda kuti atumize antchito kukakolola.”+
10 Choncho anaitana ophunzira ake 12 nʼkuwapatsa mphamvu kuti azitha kutulutsa mizimu yoipa+ komanso kuchiritsa matenda a mtundu uliwonse amene anthu ankadwala.
2 Mayina a atumwi 12 ndi awa:+ Simoni, amene ankatchulidwa kuti Petulo*+ ndi Andireya+ mchimwene wake. Yakobo mwana wa Zebedayo ndi mchimwene wake Yohane.+ 3 Filipo ndi Batolomeyo,+ Tomasi+ ndi Mateyu+ wokhometsa msonkho, Yakobo mwana wa Alifeyo ndi Tadeyo. 4 Simoni Kananiya* ndi Yudasi Isikariyoti, amene pambuyo pake anapereka Yesu.+
5 Yesu anatumiza atumwi 12 amenewa ndipo anawapatsa malangizo awa:+ “Musapite mumsewu wa anthu a mitundu ina ndipo musalowe mumzinda uliwonse wa Asamariya.+ 6 Mʼmalomwake, nthawi zonse muzipita kwa nkhosa zosochera za nyumba ya Isiraeli.+ 7 Mukapita muzikalalikira kuti, ‘Ufumu wakumwamba wayandikira.’+ 8 Muzichiritsa odwala,+ kuukitsa anthu akufa, kuyeretsa akhate komanso kutulutsa ziwanda. Munalandira kwaulere, muzipereka kwaulere. 9 Musatenge golide, siliva kapena kopa* mʼzikwama zanu za ndalama.+ 10 Musatenge thumba la chakudya cha pa ulendo kapena malaya awiri* kapena nsapato kapenanso ndodo+ chifukwa wantchito ayenera kulandira chakudya chake.+
11 Mukalowa mumzinda kapena mʼmudzi uliwonse, muzifufuza yemwe ali woyenerera kumuuza uthenga wanu, ndipo muzikhala mʼnyumba yake mpaka nthawi yochoka.+ 12 Mukalowa mʼnyumba, muzipereka moni kwa anthu a mʼbanjamo. 13 Ngati akulandirani bwino, mtendere umene mukuwafunira ukhale pa anthuwo,+ koma ngati sanakulandireni bwino, mtendere wanu ubwerere kwa inu. 14 Kulikonse kumene munthu sakakulandirani kapena kumvetsera mawu anu, mukamatuluka mʼnyumba imeneyo kapena mumzinda umenewo muzisansa fumbi kumapazi anu.+ 15 Ndithu ndikukuuzani, chilango cha mzinda umenewo chidzakhala chopweteka kwambiri pa Tsiku la Chiweruzo kuposa cha Sodomu ndi Gomora.+
16 Taonani! Ndikukutumizani ngati nkhosa pakati pa mimbulu. Choncho muzichita zinthu mochenjera ngati njoka koma moona mtima ngati nkhunda.+ 17 Chenjerani ndi anthu, chifukwa adzakutengerani kumakhoti aangʼono,+ ndipo adzakukwapulani+ mumasunagoge awo.+ 18 Adzakupititsani kwa abwanamkubwa ndi mafumu+ chifukwa ndinu otsatira anga, kuti iwowo komanso anthu a mitundu ina aphunzire za ine.+ 19 Koma akadzakupititsani kumeneko, musadzade nkhawa kuti mudzalankhula bwanji kapena kuti mudzanena chiyani, chifukwa zoti mulankhule mudzapatsidwa nthawi yomweyo.+ 20 Zili choncho chifukwa wolankhula simudzakhala inu nokha, koma mzimu wa Atate wanu udzalankhula kudzera mwa inu.+ 21 Komanso munthu adzapereka mʼbale wake kuti aphedwe ndipo bambo adzapereka mwana wake. Ana adzaukira makolo awo ndipo adzachititsa kuti aphedwe.+ 22 Anthu onse adzadana nanu chifukwa cha dzina langa,+ koma amene adzapirire* mpaka mapeto ndi amene adzapulumuke.+ 23 Akakuzunzani mumzinda umodzi, muthawire mumzinda wina.+ Ndithu ndikukuuzani, simudzamaliza kuzungulira mizinda yonse ya Isiraeli Mwana wa munthu asanafike.
24 Wophunzira saposa mphunzitsi wake ndipo kapolo saposa mbuye wake.+ 25 Wophunzira amangofanana ndi mphunzitsi wake ndipo kapolo amangofanana ndi mbuye wake.+ Ngati anthu atchula mwininyumba kuti Belezebule,*+ kuli bwanji ena a mʼbanja lakelo? 26 Choncho musawaope, chifukwa palibe chobisika chimene sichidzaululika ndipo palibe chinsinsi chimene sichidzadziwika.+ 27 Zimene ndimakuuzani mumdima, muzinene poyera, ndipo zimene mumamva anthu akunongʼonezana, muzilalikire muli padenga.+ 28 Musachite mantha ndi amene amapha thupi koma sangathe kupha moyo.+ Mʼmalomwake, muziopa amene angathe kuwononga zonse ziwiri, moyo ndi thupi lomwe mʼGehena.*+ 29 Mpheta ziwiri amazigulitsa kakhobidi kamodzi kochepa mphamvu,* si choncho? Koma palibe ngakhale imodzi imene idzagwa pansi Atate wanu osadziwa.+ 30 Ndipotu ngakhale tsitsi lonse lamʼmutu mwanu amaliwerenga. 31 Choncho musachite mantha, ndinu ofunika kwambiri kuposa mpheta zambiri.+
32 Choncho aliyense amene akuvomereza pamaso pa anthu kuti ndi wophunzira wanga,+ inenso ndidzamuvomereza pamaso pa Atate wanga wakumwamba kuti ndi wophunzira wanga.+ 33 Koma aliyense amene adzandikane pamaso pa anthu, inenso ndidzamukana pamaso pa Atate wanga wakumwamba.+ 34 Musaganize kuti ndinabwera kudzabweretsa mtendere padziko lapansi. Sindinabwere kuti ndidzabweretse mtendere koma lupanga.+ 35 Ndinabwera kudzagawanitsa anthu. Ndinabwera kudzachititsa kuti mwana wamwamuna atsutsane ndi bambo ake, mwana wamkazi atsutsane ndi mayi ake ndiponso kuti mkazi wokwatiwa atsutsane ndi apongozi ake aakazi.+ 36 Kunena zoona, adani a munthu adzakhala a mʼbanja lake lenileni. 37 Aliyense amene amakonda kwambiri bambo ake kapena mayi ake kuposa ine ndi wosayenera kuti akhale wophunzira wanga. Komanso aliyense amene amakonda kwambiri mwana wake wamwamuna kapena wamkazi kuposa ine ndi wosayenera kuti akhale wophunzira wanga.+ 38 Ndiponso aliyense amene sakufuna kunyamula mtengo wake wozunzikirapo* nʼkupitiriza kunditsatira ndi wosayenera kuti akhale wophunzira wanga.+ 39 Aliyense amene akuyesa kupulumutsa moyo wake adzautaya, koma amene wataya moyo wake chifukwa cha ine adzaupeza.+
40 Amene wakulandirani walandiranso ine ndipo amene walandira ine walandiranso amene anandituma.+ 41 Amene walandira mneneri chifukwa ndi mneneri adzalandira mphoto yofanana ndi imene mneneri amalandira,+ ndipo amene walandira munthu wolungama chifukwa ndi wolungama adzalandira mphoto yofanana ndi imene munthu wolungama amalandira. 42 Aliyense wopatsa mmodzi wa tiana iti ngakhale madzi ozizira okha mʼkapu kuti amwe chifukwa ndi wophunzira wanga, ndithu ndikukuuzani, ameneyo mphoto yake sidzatayika ngakhale pangʼono.”+
11 Yesu atamaliza kupereka malangizo kwa ophunzira ake 12 aja, anachoka kumeneko nʼkupita kukaphunzitsa ndi kukalalikira kumizinda ina.+
2 Koma Yohane ali mʼndende,+ anamva zimene Khristu ankachita ndipo anatuma ophunzira ake+ 3 kukamufunsa kuti: “Kodi Mesiya amene tikumuyembekezera uja ndi inu kapena tiyembekezere wina?”+ 4 Poyankha Yesu anawauza kuti: “Pitani mukauze Yohane zimene mukumva ndi kuona:+ 5 Amene anali ndi vuto losaona akuona,+ olumala akuyenda, akhate+ akuyeretsedwa ndipo amene anali ndi vuto losamva akumva. Akufa akuukitsidwa ndipo osauka akuuzidwa uthenga wabwino.+ 6 Wosangalala ndi amene sapeza chokhumudwitsa mwa ine.”+
7 Pamene ophunzira a Yohane ankabwerera, Yesu anayamba kuuza gulu la anthu za Yohane kuti: “Kodi munapita mʼchipululu kukaona chiyani?+ Kodi munapita kukaona bango logwedezeka ndi mphepo?+ 8 Nanga munapita kukaona chiyani? Munthu wovala zovala zapamwamba kapena? Ayi, paja amene amavala zovala zapamwamba amapezeka mʼnyumba za mafumu. 9 Nangano nʼchifukwa chiyani munapita makamaka? Kukaona mneneri kapena? Inde, ndikukuuzani, Yohane ndi mneneri komanso ndi wofunika kwambiri kuposa aneneri.+ 10 Malemba amanena za iyeyu kuti: ‘Taona! Ine ndikutumiza mthenga wanga kuti atsogole kukakukonzera njira!’+ 11 Ndithu ndikukuuzani, pa anthu onse,* palibe wamkulu kuposa Yohane Mʼbatizi. Koma munthu amene ali wocheperapo mu Ufumu wakumwamba ndi wamkulu kuposa iyeyu.+ 12 Kuyambira mʼmasiku a Yohane Mʼbatizi mpaka pano anthu akuyesetsa mwakhama kuti apeze mwayi wolowa mu Ufumu wakumwamba, ndipo amene akuyesetsa mwakhama akuupeza.+ 13 Chifukwa zonse zimene aneneri analemba komanso Chilamulo, zinalosera mpaka nthawi ya Yohane.+ 14 Kaya mukhulupirira kapena ayi, Yohane ndi ‘Eliya amene aneneri ananena kuti adzabwera.’+ 15 Amene ali ndi makutu amve.
16 Kodi mʼbadwo uwu ndiuyerekezere ndi ndani?+ Uli ngati ana aangʼono amene akhala pansi mʼmisika nʼkumafuulira anzawo amene amasewera nawo 17 kuti: ‘Tinakuimbirani chitoliro, koma simunavine. Tinalira mofuula, koma inu simunadzigugude pachifuwa chifukwa cha chisoni.’ 18 Mofanana ndi zimenezi, Yohane anabwera ndipo sankadya kapena kumwa. Koma anthu ankanena kuti, ‘Ali ndi chiwanda.’ 19 Kunabwera Mwana wa munthu ndipo akudya ndi kumwa+ koma anthu akunena kuti, ‘Taonani! Munthu wosusuka ndi wokonda kwambiri vinyo, bwenzi la okhometsa msonkho ndi ochimwa.’+ Mulimonsemo, nzeru imatsimikizirika kuti ndi yolungama* chifukwa cha ntchito zake.”*+
20 Kenako anayamba kudzudzula mizinda imene anachitamo ntchito zambiri zamphamvu chifukwa sinalape. Iye anati: 21 “Tsoka kwa iwe Korazini! Tsoka kwa iwe Betsaida! Chifukwa ntchito zamphamvu zimene zinachitika mwa iwe zikanachitika ku Turo ndi ku Sidoni, anthu akanakhala atalapa kalekale, atavala ziguduli nʼkukhala paphulusa.+ 22 Koma ndikukuuzani kuti chilango chanu chidzakhala chopweteka kwambiri kuposa cha Turo ndi Sidoni pa Tsiku la Chiweruzo.+ 23 Iwenso Kaperenao,+ kodi mwina udzakwezedwa kumwamba? Ayi, koma udzatsikira ku Manda,*+ chifukwa ntchito zamphamvu zimene zinachitika mwa iwe zikanachitika ku Sodomu, mzindawo ukanakhala ulipobe mpaka lero. 24 Koma ndikukuuzani kuti chilango cha Kaperenao chidzakhala chopweteka kwambiri kuposa cha Sodomu pa Tsiku la Chiweruzo.”+
25 Pa nthawi imeneyo Yesu ananena kuti: “Ndikukutamandani inu Atate pamaso pa onse, Ambuye wakumwamba ndi dziko lapansi, chifukwa anthu anzeru ndi ozindikira mwawabisira zinthu zimenezi ndipo mwaziulula kwa ana aangʼono.+ 26 Inde Atate, chifukwa inu munavomereza kuti zimenezi zichitike. 27 Atate wanga wapereka zinthu zonse kwa ine+ ndipo palibe amene akumudziwa bwino Mwana koma Atate okha.+ Komanso palibe amene akuwadziwa bwino Atate koma Mwana yekha ndi aliyense amene Mwanayo wafuna kumuululira za Atatewo.+ 28 Bwerani kwa ine inu nonse amene mukugwira ntchito yotopetsa ndi olemedwa ndipo ndidzakutsitsimulani. 29 Senzani goli langa ndipo lolani kuti ndikuphunzitseni, chifukwa ndine wofatsa ndi wodzichepetsa+ ndipo mudzatsitsimulidwa. 30 Chifukwa goli langa ndi losavuta kunyamula ndipo katundu wanga ndi wopepuka.”
12 Pa nthawi ina, Yesu ankadutsa mʼminda ya tirigu pa tsiku la Sabata. Ophunzira ake anamva njala ndipo anayamba kubudula ngala za tirigu nʼkumadya.+ 2 Afarisi ataona zimenezi anamuuza kuti: “Taona! Ophunzira ako akuchita zinthu zimene ndi zosayenera kuchita pa Sabata.”+ 3 Koma iye anawayankha kuti: “Kodi simunawerenge zimene Davide anachita, iyeyo ndi amuna omwe anali naye atamva njala?+ 4 Iye analowa mʼnyumba ya Mulungu ndipo anadya mitanda ya mkate woonetsa kwa Mulungu,*+ umene iye ndi anthu omwe anali nawo aja sankayenera kudya malinga ndi malamulo, koma ansembe okha.+ 5 Kapena kodi simunawerenge mʼChilamulo kuti ansembe mʼkachisi ankaphwanya Sabata pogwira ntchito tsiku la Sabata koma nʼkukhalabe osalakwa?+ 6 Koma ndikukuuzani kuti winawake wamkulu kuposa kachisi ali pano.+ 7 Komabe, ngati mukanamvetsa tanthauzo la mawu akuti, ‘Ndikufuna chifundo+ osati nsembe,’+ simukanaweruza anthu osalakwa. 8 Chifukwa Mwana wa munthu ndi Mbuye wa Sabata.”+
9 Atachoka malo amenewo, anakalowa musunagoge wawo. 10 Mmenemo munali munthu wolumala dzanja.+ Choncho iwo anamufunsa kuti, “Kodi nʼzololeka kuchiritsa odwala pa tsiku la Sabata?” Cholinga chawo chinali choti amupezere chifukwa nʼkumuimba mlandu.+ 11 Koma iye anawayankha kuti: “Mutakhala ndi nkhosa imodzi yokha, ndiyeno nkhosayo nʼkugwera mʼdzenje pa tsiku la Sabata, kodi alipo pakati panu amene sangaigwire nʼkuitulutsa?+ 12 Komatu munthu ndi wofunika kwambiri kuposa nkhosa! Choncho ndi zololeka kuchita chinthu chabwino pa tsiku la Sabata.” 13 Kenako anauza munthuyo kuti: “Tambasula dzanja lako.” Iye analitambasuladi ndipo linakhalanso bwinobwino ngati linzake. 14 Koma Afarisiwo anatuluka nʼkukakonza chiwembu kuti amuphe. 15 Yesu atadziwa zimenezi, anachoka pamalo amenewo. Anthu ambiri anamutsatira+ ndipo iye anawachiritsa onsewo, 16 koma anawalamula mwamphamvu kuti asamuulule.+ 17 Anachita zimenezi kuti zimene Mulungu ananena kudzera mwa mneneri Yesaya zikwaniritsidwe. Iye ananena kuti:
18 “Taonani mtumiki wanga+ amene ndamusankha, wokondedwa wanga, amene amandisangalatsa kwambiri.+ Ndidzaika mzimu wanga pa iye+ ndipo anthu a mitundu ina adzawasonyeza bwinobwino chilungamo chenicheni. 19 Sadzakangana ndi munthu+ kapena kufuula ndipo palibe amene adzamve mawu ake mʼmisewu ikuluikulu. 20 Bango lophwanyika sadzalithyola ndipo chingwe cha nyale chimene chikufuka utsi sadzachizimitsa,+ mpaka atakwanitsa kubweretsa chilungamo. 21 Ndithudi, mʼdzina lake mitundu ya anthu idzayembekezera zabwino.”+
22 Kenako anamubweretsera munthu wogwidwa ndi chiwanda, amenenso anali ndi vuto losaona komanso sankalankhula ndipo iye anamuchiritsa, moti munthu wosalankhulayo anayamba kulankhula ndiponso kuona. 23 Zitatero, gulu la anthulo linadabwa kwambiri ndipo anayamba kunena kuti: “Kodi ameneyu sangakhale Mwana wa Davide uja?” 24 Afarisi atamva zimenezi ananena kuti: “Ameneyutu sikuti amatulutsa ziwanda ndi mphamvu zake ayi koma ndi mphamvu za Belezebule,* wolamulira ziwanda.”+ 25 Atadziwa maganizo awo, iye anawauza kuti: “Ufumu uliwonse wogawanika umatha ndipo mzinda kapena nyumba iliyonse yogawanika sikhalitsa. 26 Mofanana ndi zimenezi, ngati Satana amatulutsa Satana, ndiye kuti wagawanika. Nanga tsopano ufumu wake ungakhalepo bwanji? 27 Komanso ngati ine ndimatulutsa ziwanda ndi mphamvu za Belezebule, nanga otsatira anu amazitulutsa ndi mphamvu za ndani? Nʼchifukwa chake otsatira anuwo adzakuweruzani kuti ndinu olakwa. 28 Koma ngati ine ndimatulutsa ziwanda ndi mphamvu ya mzimu wa Mulungu, ndiye kuti Ufumu wa Mulungu wakufikirani modzidzimutsa.+ 29 Kapena munthu angalowe bwanji mʼnyumba ya munthu wamphamvu nʼkumulanda katundu wake, ngati choyamba atapanda kumanga munthu wamphamvuyo? Akatero mʼpamene angathe kutenga katundu mʼnyumbamo. 30 Aliyense amene sali kumbali yanga akutsutsana ndi ine ndipo amene sagwira ntchito yosonkhanitsa anthu limodzi ndi ine amawabalalitsa.+
31 Pa chifukwa chimenechi ndikukuuzani kuti, anthu adzakhululukidwa tchimo la mtundu uliwonse ndi mawu aliwonse onyoza, koma wonyoza mzimu sadzakhululukidwa.+ 32 Mwachitsanzo, aliyense wolankhula mawu onyoza Mwana wa munthu, adzakhululukidwa.+ Koma aliyense wolankhula mawu onyoza mzimu woyera, sadzakhululukidwa, mʼnthawi* ino kapena ikubwerayo.+
33 Inu mumachititsa kuti mtengo ndi zipatso zake zikhale zabwino kapena mumachititsa kuti mtengo ndi zipatso zake zikhale zovunda, chifukwa mtengo umadziwika ndi zipatso zake.+ 34 Ana a njoka inu,+ mungalankhule bwanji zinthu zabwino pamene muli oipa? Chifukwa pakamwa pamalankhula zosefukira mumtima.+ 35 Munthu wabwino amatulutsa zabwino mʼchuma chabwino chamumtima mwake, koma munthu woipa amatulutsa zoipa mʼchuma choipa chamumtima mwake.+ 36 Ndikukuuzani kuti pa Tsiku la Chiweruzo, anthu adzayankha mlandu+ pa mawu aliwonse opanda pake amene iwo amalankhula. 37 Chifukwa ndi mawu ako udzaweruzidwa kuti ndiwe wolungama ndipo ndi mawu akonso udzaweruzidwa kuti ndiwe wolakwa.”
38 Ndiyeno alembi ndi Afarisi ena anamupempha kuti: “Mphunzitsi, tikufuna mutionetse chizindikiro.”+ 39 Poyankha iye anawauza kuti: “Mʼbadwo woipa komanso wachigololo* ukufunitsitsa utaona chizindikiro. Koma sudzapatsidwa chizindikiro chilichonse kupatulapo chizindikiro cha mneneri Yona chokha.+ 40 Chifukwa mofanana ndi Yona amene anakhala mʼmimba mwa chinsomba chachikulu masiku atatu, masana ndi usiku,+ Mwana wa munthu nayenso adzakhala mumtima wa dziko lapansi masiku atatu, masana ndi usiku.+ 41 Anthu a ku Nineve adzauka pa Tsiku la Chiweruzo limodzi ndi mʼbadwo uwu ndipo adzautsutsa, chifukwa iwo analapa atamva ulaliki wa Yona.+ Koma tsopano wina woposa Yona ali pano.+ 42 Mfumukazi yakumʼmwera adzaiukitsa kwa akufa pa Tsiku la Chiweruzo limodzi ndi mʼbadwo uwu ndipo idzautsutsa, chifukwa mfumukazi imeneyi inabwera kuchokera kumalekezero a dziko lapansi kudzamva nzeru za Solomo.+ Koma tsopano wina woposa Solomo ali pano.+
43 Mzimu wonyansa ukatuluka mwa munthu, umadutsa mʼmalo opanda madzi kufunafuna malo okhala ndipo supeza aliwonse.+ 44 Ndiyeno umati, ‘Ndibwerera kunyumba yanga imene ndinatulukamo ija.’ Ukafika umapeza kuti simukukhala aliyense koma ndi mosesedwa bwino komanso mokongoletsedwa. 45 Ukatero umapita kukatenga mizimu ina 7 yoipa kwambiri kuposa umenewo ndipo ikalowa mkatimo imakhala mmenemo. Zotsatira zake, zochita za munthuyo zimakhala zoipa kwambiri kuposa poyamba.+ Ndi mmenenso zidzakhalire ndi mʼbadwo woipawu.”
46 Ali mkati molankhula ndi gulu la anthulo, kunabwera mayi ake ndi azichimwene ake.+ Iwo anaima panja ndipo ankafuna kuti alankhule naye.+ 47 Choncho munthu wina anamuuza kuti: “Mayi anu ndi azichimwene anu aima panjapa, akufuna kulankhula nanu.” 48 Poyankha iye anauza munthu amene ankalankhula nayeyo kuti: “Kodi mayi anga ndi ndani ndipo azichimwene anga ndi ndani?” 49 Kenako anatambasula dzanja lake ndi kuloza ophunzira ake, nʼkunena kuti: “Ona! Mayi anga ndi azichimwene anga ndi awa!+ 50 Chifukwa aliyense amene amachita zimene Atate wanga wakumwamba amafuna, ameneyo ndi mchimwene wanga, mchemwali wanga ndi mayi anga.”+
13 Tsiku limenelo, Yesu anachoka kunyumba nʼkukakhala pansi mʼmphepete mwa nyanja. 2 Gulu lalikulu la anthu linasonkhana pamene iye anali, moti iye anakwera mʼngalawa nʼkukhala pansi, ndipo gulu lonse la anthulo linaimirira mʼmphepete mwa nyanjayo.+ 3 Kenako anawauza zinthu zambiri pogwiritsa ntchito mafanizo+ kuti: “Tamverani! Wofesa mbewu anapita kukafesa mbewu.+ 4 Pamene ankafesa, mbewu zina zinagwera mʼmbali mwa msewu ndipo kunabwera mbalame nʼkuzidya.+ 5 Zina zinagwera pamiyala pamene panalibe dothi lokwanira ndipo zinamera mwamsanga chifukwa dothilo linali losazama.+ 6 Koma dzuwa litawala kwambiri zinawauka ndipo zinafota chifukwa zinalibe mizu. 7 Mbewu zina zinagwera paminga ndipo mingazo zinakula nʼkulepheretsa mbewuzo kukula.+ 8 Koma zina zinagwera panthaka yabwino ndipo zinayamba kubereka zipatso. Mbewu ina inabereka zipatso 100, ina 60 ndipo ina 30.+ 9 Amene ali ndi makutu amve.”+
10 Ndiyeno ophunzira ake anabwera nʼkumufunsa kuti: “Nʼchifukwa chiyani mukulankhula nawo pogwiritsa ntchito mafanizo?”+ 11 Koma iye anawayankha kuti: “Inu mwapatsidwa mwayi woti mumvetse zinsinsi zopatulika+ za Ufumu wakumwamba, koma anthu amenewa sanapatsidwe mwayi umenewo. 12 Chifukwa amene ali nazo, adzapatsidwa zinanso zambiri ndipo adzakhala ndi zochuluka. Koma amene alibe, adzalandidwa ngakhale zimene akuganiza kuti ali nazo.+ 13 Nʼchifukwa chake ndikulankhula nawo pogwiritsa ntchito mafanizo. Chifukwa ngakhale kuti akuyangʼana, sakuona chilichonse. Ngakhale kuti akumva, sakumvetsa zimene zikunenedwa ndipo sakuzindikira tanthauzo lake.+ 14 Ulosi wa Yesaya ukukwaniritsidwa pa iwowa. Ulosiwo umanena kuti: ‘Kumva mudzamva ndithu, koma simudzazindikira tanthauzo lake. Kuyangʼana mudzangʼana ndithu, koma simudzaona chilichonse.+ 15 Chifukwa anthu awa aumitsa mitima yawo ndipo amva ndi makutu awo koma osalabadira. Atseka maso awo kuti asaone ndi maso awo komanso kuti asamve ndi makutu awo nʼkuzindikira tanthauzo lake mʼmitima yawo kenako nʼkutembenuka kuti ine ndiwachiritse.’+
16 Koma inu ndinu osangalala chifukwa maso anu amaona komanso makutu anu amamva.+ 17 Chifukwa ndithu ndikukuuzani, aneneri ambiri komanso anthu olungama ankalakalaka kuti aone zinthu zimene mukuziona inuzi koma sanazione,+ komanso kuti amve zimene mukumva inuzi koma sanazimve.
18 Tsopano mvetserani fanizo la munthu wofesa mbewu.+ 19 Munthu aliyense akamva mawu a Ufumu koma osazindikira tanthauzo lake, woipayo+ amabwera nʼkuchotsa zimene zafesedwa mumtima wa munthuyo. Iyi ndi mbewu imene inafesedwa mʼmbali mwa msewu ija.+ 20 Koma imene inafesedwa pamiyala, ndi munthu amene wamva mawu nʼkuwavomereza mwamsanga ndiponso mosangalala.+ 21 Komabe chifukwa chakuti amakhala alibe mizu amapitiriza kukula kwa nthawi yochepa. Koma akakumana ndi masautso kapena kuyamba kuzunzidwa chifukwa cha mawuwo, iye amapunthwa mwamsanga. 22 Imene inafesedwa paminga, ndi munthu amene amamva mawu, koma nkhawa za moyo wa mʼnthawi* ino+ ndiponso chinyengo champhamvu cha chuma zimalepheretsa mawuwo kukula ndipo sabereka zipatso.+ 23 Koma mbewu imene inafesedwa panthaka yabwino, ndi munthu amene wamva mawu nʼkuzindikira tanthauzo lake, amene amaberekadi zipatso, wina amabereka zipatso 100, wina 60 ndipo wina 30.”+
24 Anawafotokozera fanizo linanso kuti: “Ufumu wakumwamba tingauyerekezere ndi munthu amene anafesa mbewu yabwino mʼmunda mwake. 25 Koma anthu ali mʼtulo, kunabwera mdani wake kudzafesa namsongole mʼmunda wa tiriguwo nʼkuchoka. 26 Tiriguyo atakula nʼkutulutsa ngala, namsongole nayenso anaonekera. 27 Ndiyeno akapolo a mwinimunda uja anabwera nʼkudzamuuza kuti, ‘Ambuye, kodi mʼmesa munafesa mbewu zabwino mʼmunda mwanu? Nanga namsongole wachokeranso kuti?’ 28 Iye anawauza kuti, ‘Munthu wina wodana nane anachita zimenezi.’+ Akapolowo anati, ‘Ndiye kodi mukufuna kuti tipite tikamuzule?’ 29 Koma iye anawayankha kuti, ‘Ayi, kuopera kuti pozula namsongoleyo mungazule limodzi ndi tirigu. 30 Zisiyeni zonse zikulire limodzi mpaka nthawi yokolola. Mʼnyengo yokolola ndidzauza okolola kuti: Choyamba sonkhanitsani namsongole nʼkumumanga mʼmitolo kuti akawotchedwe. Kenako musonkhanitse tirigu mʼnyumba yanga yosungiramo zinthu.’”+
31 Anawauzanso fanizo lina kuti: “Ufumu wakumwamba uli ngati kanjere ka mpiru* kamene munthu anakatenga nʼkukadzala mʼmunda mwake.+ 32 Kanjere kameneka ndi kakangʼono kwambiri kuposa njere zonse, koma kakamera kamakula kwambiri kuposa mbewu zonse zakudimba ndipo umakhala mtengo, moti mbalame zamumlengalenga zimabwera kudzapeza malo okhala munthambi zake.”
33 Anawafotokozeranso fanizo lina kuti: “Ufumu wakumwamba uli ngati zofufumitsa zimene mkazi wina anazitenga nʼkuzisakaniza ndi ufa wokwana mabeseni atatu akuluakulu oyezera, ndipo mtanda wonsewo unafufuma.”+
34 Yesu analankhula zonsezi ndi gulu la anthulo pogwiritsa ntchito mafanizo. Ndithudi, nthawi zonse iye ankalankhula nawo pogwiritsa ntchito mafanizo,+ 35 kuti zimene Mulungu ananena kudzera mwa mneneri zikwaniritsidwe. Mneneriyo anati: “Ndidzatsegula pakamwa panga nʼkunena mafanizo. Ndidzafalitsa zinthu zimene zinabisika kuchokera pachiyambi.”*+
36 Kenako atauza gulu la anthulo kuti lizipita, analowa mʼnyumba. Ndipo ophunzira ake anabwera kwa iye nʼkunena kuti: “Timasulireni fanizo lija la namsongole mʼmunda.” 37 Poyankha iye ananena kuti: “Amene anafesa mbewu yabwino uja ndi Mwana wa munthu. 38 Munda ndi dziko+ ndipo mbewu yabwino ndi ana a Ufumu. Koma namsongole ndi ana a woipayo,+ 39 ndipo mdani amene anafesa namsongole ndi Mdyerekezi. Nthawi yokolola ikuimira mapeto a nthawi* ino ndipo okololawo ndi angelo. 40 Mofanana ndi namsongole amene amamusonkhanitsa nʼkumuwotcha pamoto, zidzakhalanso choncho pamapeto a nthawi* ino.+ 41 Mwana wa munthu adzatumiza angelo ake ndipo adzachotsa mu Ufumu wake zinthu zonse zopunthwitsa ndiponso anthu osamvera malamulo. 42 Kenako adzawaponya mungʼanjo yamoto.+ Kumeneko adzalira ndi kukukuta mano. 43 Pa nthawi imeneyo olungama adzawala kwambiri ngati dzuwa+ mu Ufumu wa Atate wawo. Amene ali ndi makutu amve.
44 Ufumu wakumwamba uli ngati chuma chobisika mʼmunda, chimene munthu anachipeza nʼkuchibisa. Chifukwa cha chimwemwe chimene anali nacho, anapita kukagulitsa zinthu zonse zimene anali nazo nʼkukagula mundawo.+
45 Komanso Ufumu wakumwamba uli ngati wamalonda woyendayenda amene akufunafuna ngale zabwino. 46 Atapeza ngale imodzi yamtengo wapatali, anapita ndipo mwamsanga anakagulitsa zinthu zonse zimene anali nazo nʼkukagula ngaleyo.+
47 Ndiponso Ufumu wakumwamba uli ngati khoka limene laponyedwa mʼnyanja ndipo likusonkhanitsa nsomba zamitundumitundu. 48 Likadzaza amalikokera kumtunda ndipo amakhala pansi nʼkumasankha zabwino+ ndi kuziika mʼmitanga, koma zosafunika+ amazitaya. 49 Ndi mmenenso zidzakhalire pamapeto a nthawi* ino. Angelo adzapita nʼkukachotsa oipa pakati pa olungama 50 ndipo adzawaponya mungʼanjo yamoto. Kumeneko adzalira ndi kukukuta mano.
51 Kodi mukumvetsa tanthauzo la zinthu zonsezi?” Iwo anamuyankha kuti: “Inde.” 52 Kenako anawauza kuti: “Popeza kuti zili choncho, mphunzitsi aliyense amene waphunzitsidwa za Ufumu wakumwamba ali ngati munthu yemwe ndi mwininyumba, amene amatulutsa zinthu zatsopano ndi zakale mosungiramo chuma chake.”
53 Yesu atamaliza kunena mafanizo amenewa anachoka kumeneko. 54 Atafika mʼdera lakwawo+ anayamba kuwaphunzitsa musunagoge wawo, moti anthu anadabwa ndipo ananena kuti: “Kodi munthu ameneyu, nzeru ndi ntchito zamphamvu zoterezi anazitenga kuti?+ 55 Kodi uyu si mwana wa kalipentala uja?+ Kodi mayi ake si Mariya, ndipo azichimwene ake si Yakobo, Yosefe, Simoni ndi Yudasi?+ 56 Ndipo azichemwali ake onse sitili nawo konkuno? Nanga iyeyu zinthu zonsezi anazitenga kuti?”+ 57 Choncho anayamba kukhumudwa naye.+ Koma Yesu anawauza kuti: “Mneneri salemekezedwa kwawo kapena mʼnyumba mwake, koma kwina.”+ 58 Ndipo sanachite ntchito zamphamvu zambiri kumeneko chifukwa chakuti anthuwo analibe chikhulupiriro.
14 Pa nthawiyo Herode, wolamulira chigawo,* anamva za Yesu+ 2 ndipo anauza atumiki ake kuti: “Ameneyu ndi Yohane Mʼbatizi. Anauka kwa akufa ndiye nʼchifukwa chake akuchita ntchito zamphamvu.”+ 3 Herode* anagwira Yohane nʼkumumanga ndipo anamutsekera mʼndende chifukwa cha Herodiya, mkazi wa mchimwene wake Filipo amene Herodeyo anakwatira.+ 4 Anachita zimenezi chifukwa Yohane ankamuuza kuti: “Nʼzosaloleka kuti mutenge mkazi ameneyu kukhala mkazi wanu.”+ 5 Komabe, ngakhale kuti Herode ankafuna kupha Yohane, ankaopa gulu la anthu chifukwa iwo ankakhulupirira kuti anali mneneri.+ 6 Koma tsiku lokumbukira kubadwa kwa Herode+ litafika, mwana wamkazi wa Herodiya anavina pa tsikulo ndipo anasangalatsa kwambiri Herode,+ 7 moti anachita kulumbira polonjeza mtsikanayo kuti adzamupatsa chilichonse chimene angapemphe. 8 Ndiyeno mtsikanayo, mayi ake atachita kumuuza zoti apemphe ananena kuti: “Mundipatse mutu wa Yohane Mʼbatizi mʼmbale pompano.”+ 9 Mfumuyo inamva chisoni koma poganizira lumbiro limene inapanga lija komanso anthu amene anali nawo paphwandolo, analamula kuti mutuwo uperekedwe. 10 Choncho anatuma munthu kuti akadule mutu wa Yohane mʼndende. 11 Kenako anabweretsa mutuwo mʼmbale nʼkuupereka kwa mtsikanayo ndipo iye anapita nawo kwa mayi ake. 12 Pambuyo pake ophunzira ake anabwera kudzatenga mtembo wake nʼkukauika mʼmanda. Kenako anapita kukauza Yesu. 13 Yesu atamva zimenezi, anachoka kumeneko pangalawa nʼkupita kumalo kopanda anthu kuti akakhale payekha. Koma gulu la anthu litamva zimenezo, linamutsatira wapansi kuchokera mʼmizinda yawo.+
14 Yesu atatsika mʼngalawayo anaona gulu lalikulu la anthu ndipo anawamvera chisoni+ nʼkuwachiritsira anthu awo odwala.+ 15 Koma chakumadzulo ophunzira ake anabwera kwa iye nʼkunena kuti: “Kuno nʼkopanda anthu ndipo nthawi yatha, auzeni anthuwa kuti anyamuke, apite mʼmidzimo kuti akagule chakudya choti adye.”+ 16 Koma Yesu anawayankha kuti: “Palibe chifukwa choti apitire. Inuyo muwapatse chakudya.” 17 Iwo anamuuza kuti: “Tilibe chilichonse pano, kupatulapo mitanda 5 ya mkate ndi nsomba ziwiri zokha basi.” 18 Iye anati: “Bweretsani zimenezo kuno.” 19 Kenako analamula gulu la anthulo kuti likhale pansi pa udzu. Ndiyeno anatenga mitanda ya mkate 5 ndi nsomba ziwiri zija nʼkuyangʼana kumwamba ndi kupemphera.+ Atatero ananyemanyema mitanda ya mkate ija nʼkuipereka kwa ophunzirawo ndipo iwo anagawira gulu la anthulo. 20 Choncho onse anadya nʼkukhuta ndipo zimene zinatsala anazitolera moti zinadzaza madengu 12.+ 21 Koma amene anadya anali amuna pafupifupi 5,000 osawerengera akazi ndi ana aangʼono.+ 22 Kenako mwamsanga, Yesu anauza ophunzira ake kuti akwere ngalawa nʼkutsogola kupita kutsidya lina. Koma iye anatsalira nʼcholinga choti auze anthuwo kuti azipita kwawo.+
23 Atauza anthuwo kuti azipita, anakwera phiri yekhayekha kukapemphera.+ Iye anakhala kumeneko yekhayekha mpaka kunja kunada. 24 Pa nthawiyi nʼkuti ngalawa ija itapita kutali* pakati pa madzi, ndipo inkakankhidwa mwamphamvu ndi mafunde chifukwa ankalimbana ndi mphepo yamphamvu. 25 Koma pa ulonda wa 4* mʼbandakucha, iye anafika kwa ophunzirawo akuyenda pamwamba pa madzi. 26 Ophunzirawo atamuona akuyenda panyanjapo, anachita mantha nʼkunena kuti: “Amenewa ndi masomphenya ndithu!” Ndipo anafuula mwamantha. 27 Koma nthawi yomweyo Yesu anawauza kuti: “Mtima mʼmalo, ndine. Musachite mantha.”+ 28 Ndiyeno Petulo anayankha kuti: “Ambuye, ngati ndinudi ndiuzeni ndiyende pamadzipa ndibwere kuli inuko.” 29 Iye anamuuza kuti: “Bwera!” Choncho Petulo anatsika mʼngalawamo nʼkuyenda pamadzi kupita kumene kunali Yesu. 30 Koma ataona mphepo yamkuntho, anachita mantha. Atayamba kumira anafuula kuti: “Ambuye, ndipulumutseni!” 31 Nthawi yomweyo Yesu anatambasula dzanja lake nʼkumugwira ndipo anamuuza kuti: “Wachikhulupiriro chochepa iwe, nʼchifukwa chiyani wakayikira?”+ 32 Atakwera mʼngalawa, mphepo yamkuntho ija inasiya. 33 Pamenepo amene anali mʼngalawamo anamugwadira nʼkunena kuti: “Ndinudi Mwana wa Mulungu.” 34 Ndipo anawolokera kumtunda ku Genesareti.+
35 Anthu amʼdera limeneli atamuzindikira, anatumiza uthenga mʼmidzi yonse yapafupi ndipo anamubweretsera anthu onse amene ankadwala. 36 Anthu ankamupempha kuti angogwira ulusi wopota wamʼmphepete mwa malaya ake akunja,+ ndipo anthu onse amene anaugwira anachiriratu.
15 Kenako Afarisi ndi alembi+ ochokera ku Yerusalemu anapita kwa Yesu nʼkumufunsa kuti: 2 “Nʼchifukwa chiyani ophunzira anu amaphwanya miyambo ya makolo? Mwachitsanzo, sasamba mʼmanja* akafuna kudya chakudya.”+
3 Koma iye anawayankha kuti: “Nʼchifukwa chiyani inuyo mumaphwanya malamulo a Mulungu chifukwa cha miyambo yanu?+ 4 Mwachitsanzo, Mulungu ananena kuti, ‘Muzilemekeza bambo anu ndi mayi anu.’+ Komanso anati, ‘Aliyense wolankhula mawu achipongwe kwa bambo ake kapena mayi ake aziphedwa.’+ 5 Koma inu mumanena kuti, ‘Aliyense wouza bambo ake kapena mayi ake kuti: “Chilichonse chimene ndili nacho, chimene ndikanakuthandizani nacho ndi mphatso yoti ndipereke kwa Mulungu,”+ 6 sakuyenera kuthandiza bambo ake.’ Choncho mwachititsa kuti mawu a Mulungu akhale opanda pake chifukwa cha miyambo yanu.+ 7 Anthu achinyengo inu! Yesaya analosera zolondola zokhudza inu pamene anati:+ 8 ‘Anthu awa amandilemekeza ndi milomo yokha, koma mitima yawo aiika kutali ndi ine. 9 Chilichonse chomwe amachita pondilambira ndi chopanda pake, chifukwa amaphunzitsa malamulo a anthu ngati kuti ndi malamulo a Mulungu.’”+ 10 Atanena zimenezi, anaitana gulu la anthu kuti liyandikire ndipo anawauza kuti: “Mvetserani ndipo muzindikire tanthauzo lake:+ 11 Chimene chimalowa mʼkamwa mwa munthu si chimene chimamuipitsa, koma chimene chimatuluka mʼkamwa mwake nʼchimene chimamuipitsa.”+
12 Ndiyeno ophunzira ake anabwera nʼkumufunsa kuti: “Kodi mukudziwa kuti Afarisi akhumudwa ndi zimene mwanena zija?”+ 13 Koma iye anayankha kuti: “Mbewu iliyonse imene sinadzalidwe ndi Atate wanga wakumwamba idzazulidwa. 14 Asiyeni amenewo. Iwo ndi atsogoleri akhungu. Choncho ngati munthu wakhungu akutsogolera wakhungu mnzake, onse awiri adzagwera mʼdzenje.”+ 15 Ndiyeno Petulo anamupempha kuti: “Timasulireni fanizo lija.” 16 Yesu anawafunsa kuti: “Kodi inunso simunamvetse?+ 17 Kodi simukudziwa kuti chilichonse chimene chalowa mʼkamwa chimadutsa mʼmimba ndipo chimakatayidwa kuchimbudzi? 18 Koma chilichonse chimene chimatuluka pakamwa chimachokera mumtima ndipo zinthu zimenezo ndi zimene zimaipitsa munthu.+ 19 Mwachitsanzo, mumtima mumachokera maganizo oipa awa:+ maganizo a kupha anthu, a chigololo, a chiwerewere,* a kuba, maumboni onama komanso kunyoza Mulungu. 20 Zimenezi ndi zinthu zimene zimaipitsa munthu, koma kudya chakudya osasamba mʼmanja* sikuipitsa munthu.”
21 Yesu atachoka kumeneko anapita mʼzigawo za Turo ndi Sidoni.+ 22 Ndiyeno kunabwera mayi wina wa ku Foinike kuchokera mʼzigawo zimenezo ndipo anafuula kuti: “Ndichitireni chifundo Ambuye, Mwana wa Davide. Mwana wanga wamkazi anagwidwa ndi chiwanda chimene chikumuzunza mwankhanza.”+ 23 Koma iye sanamuyankhe chilichonse. Choncho ophunzira ake anabwera nʼkumuuza kuti: “Muuzeni kuti azipita, chifukwa akupitirizabe kufuula mʼmbuyo mwathumu.” 24 Iye anayankha kuti: “Ine sananditumize kwa wina aliyense koma kwa nkhosa zotayika za nyumba ya Isiraeli.”+ 25 Koma mayi uja anabwera pafupi nʼkumugwadira ndipo ananena kuti: “Ambuye, ndithandizeni!” 26 Iye anamuyankha kuti: “Si bwino kutenga chakudya cha ana nʼkuponyera tiagalu.” 27 Mayiyo ananena kuti: “Inde Ambuye, komatu tiagalu timadya nyenyeswa zimene zikugwa patebulo la ambuye awo.”+ 28 Ndiyeno Yesu anamuyankha kuti: “Mayi iwe, chikhulupiriro chako ndi chachikulu. Zimene ukufuna zichitike kwa iwe.” Ndipo nthawi yomweyo mwana wake anachira.
29 Yesu atachoka kumeneko, anapita kufupi ndi nyanja ya Galileya+ ndipo anakwera phiri nʼkukakhala pansi mʼphirimo. 30 Kenako anthu ochuluka anabwera kwa iye. Anabwera ndi anthu olumala, othyoka ziwalo, a vuto losaona, a vuto losalankhula, ndi ena ambiri osiyanasiyana. Anthuwo anawakhazika pamapazi ake ndipo iye anawachiritsa.+ 31 Choncho gulu la anthulo linadabwa kuona anthu osalankhula akulankhula, olumala akuyenda ndiponso anthu osaona akuona ndipo anatamanda Mulungu wa Isiraeli.+
32 Koma Yesu anaitana ophunzira ake nʼkuwauza kuti: “Gulu la anthuli likundimvetsa chisoni,+ chifukwa anthuwa akhala ndi ine kwa masiku atatu ndipo alibe chakudya. Sindikufuna kuwauza kuti azipita ndi njala* chifukwa angalenguke panjira.”+ 33 Koma ophunzirawo anamuuza kuti: “Kumalo kopanda anthu ngati kuno chakudya chokwanira gulu lonseli tichipeza kuti?”+ 34 Ndiyeno Yesu anawafunsa kuti: “Muli ndi mitanda ingati ya mkate?” Iwo anayankha kuti: “Tili nayo 7 ndi tinsomba towerengeka.” 35 Choncho atauza anthuwo kuti akhale pansi, 36 anatenga mitanda 7 ya mkate ija ndi nsomba zija. Atayamika, anainyemanyema nʼkuyamba kupereka kwa ophunzirawo ndipo iwo anagawira gulu la anthulo.+ 37 Anthu onsewo anadya nʼkukhuta, moti zotsala zimene anatolera zinadzaza madengu akuluakulu 7.+ 38 Koma amene anadya anali amuna 4,000, osawerengera akazi ndi ana aangʼono. 39 Pambuyo pake, atauza anthuwo kuti azipita kwawo, iye anakwera ngalawa nʼkufika mʼchigawo cha Magadani.+
16 Kenako Afarisi ndi Asaduki anafika kwa Yesu ndipo pofuna kumuyesa, anamupempha kuti awaonetse chizindikiro chochokera kumwamba.+ 2 Koma Yesu anawayankha kuti: “Kunja kukamada mumanena kuti, ‘Nyengo ikhala yabwino, chifukwa kumwamba kwafiira ngati moto.’ 3 Koma mʼmawa mumanena kuti, ‘Lero kukuoneka kuti kugwa mvula, chifukwa kumwamba kwafiira ndipo kuli mitambo.’ Mumadziwa kumasulira kaonekedwe ka kumwamba, koma mukulephera kumasulira zizindikiro za nthawi ino. 4 Mʼbadwo woipa komanso wachigololo* ukufunitsitsabe chizindikiro, koma sudzapatsidwa chizindikiro chilichonse+ kupatulapo chizindikiro cha Yona chokha.”+ Atanena zimenezi, anachoka nʼkuwasiya.
5 Kenako ophunzira ake anawolokera kutsidya lina koma anaiwala kutenga mikate.+ 6 Ndiyeno Yesu anawauza kuti: “Khalani maso ndipo musamale ndi chofufumitsa cha Afarisi ndi Asaduki.”+ 7 Koma iwo anayamba kukambirana kuti: “Sitinatenge mikate pobwera kuno.” 8 Yesu anadziwa zimenezi ndipo ananena kuti: “Achikhulupiriro chochepa inu, nʼchifukwa chiyani mukukambirana kuti mulibe mikate? 9 Kodi mfundo yake simukuimvetsabe? Kapena kodi simukukumbukira anthu 5,000 amene anadya mitanda 5 ya mikate, komanso kuchuluka kwa madengu amene munatolera a chakudya chimene chinatsala?+ 10 Kapena kodi simukukumbukira anthu 4,000 amene anadya mitanda 7 ya mikate, komanso kuchuluka kwa madengu akuluakulu a chakudya chimene chinatsala amene munatolera?+ 11 Nanga bwanji simukuzindikira kuti sindikunena za mkate, koma zakuti musamale ndi zofufumitsa za Afarisi ndi Asaduki?”+ 12 Atatero anazindikira kuti sakunena zakuti asamale ndi zofufumitsa za mkate, koma kuti asamale ndi zimene Afarisi ndi Asaduki amaphunzitsa.
13 Atafika mʼchigawo cha Kaisareya wa Filipi, Yesu anafunsa ophunzira ake kuti: “Kodi anthu akumanena kuti Mwana wa munthu ndi ndani?”+ 14 Iwo anayankha kuti: “Ena akumanena kuti ndinu Yohane Mʼbatizi,+ ena akumati Eliya,+ koma ena akumanena kuti Yeremiya kapena mmodzi wa aneneri.” 15 Ndiyeno iye anawafunsa kuti: “Nanga inuyo mumati ndine ndani?” 16 Simoni Petulo anayankha kuti: “Ndinu Khristu,+ Mwana wa Mulungu wamoyo.”+ 17 Yesu anamuuza kuti: “Ndiwe wosangalala Simoni mwana wa Yona, chifukwa si munthu* amene wakuululira zimenezi, koma Atate wanga amene ali kumwamba ndi amene wachita zimenezi.+ 18 Choncho inenso ndikukuuza kuti: Iwe ndiwe Petulo+ ndipo pathanthwe+ ili ndidzamangapo mpingo wanga. Mageti a Manda* sadzaugonjetsa. 19 Ine ndidzakupatsa makiyi a Ufumu wakumwamba. Chilichonse chimene udzamanga padziko lapansi chidzakhala chitamangidwa kale kumwamba, ndipo chilichonse chimene udzamasula padziko lapansi chidzakhala chitamasulidwa kale kumwamba.” 20 Ndiyeno analamula ophunzirawo mwamphamvu kuti asauze aliyense kuti iye ndi Khristu.+
21 Kuyambira nthawi imeneyo, Yesu anayamba kuuza ophunzira ake kuti iyeyo akuyenera kupita ku Yerusalemu. Kumeneko akazunzidwa kwambiri ndi akulu, ansembe aakulu ndi alembi ndipo akaphedwa, koma pa tsiku lachitatu adzaukitsidwa.+ 22 Ndiyeno Petulo anatengera Yesu pambali nʼkuyamba kumudzudzula kuti: “Dzikomereni mtima Ambuye. Musalole kuti zimenezi zikuchitikireni ngakhale pangʼono.”+ 23 Koma iye anatembenuka nʼkuuza Petulo kuti: “Pita kumbuyo kwanga, Satana! Ndiwe chopunthwitsa kwa ine chifukwa zimene umaganiza si maganizo a Mulungu, koma maganizo a anthu.”+
24 Kenako Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Ngati munthu akufuna kunditsatira, adzikane yekha ndipo anyamule mtengo wake wozunzikirapo* nʼkupitiriza kunditsatira.+ 25 Chifukwa aliyense amene akufuna kupulumutsa moyo wake adzautaya, koma aliyense amene wataya moyo wake chifukwa cha ine adzaupeza.*+ 26 Kodi munthu angapindule chiyani ngati atapeza zinthu zonse zamʼdzikoli koma nʼkutaya moyo wake?+ Kapena kodi munthu angapereke chiyani choti asinthanitse ndi moyo wake?+ 27 Chifukwa Mwana wa munthu adzabwera mu ulemerero wa Atate wake limodzi ndi angelo ake. Pa nthawi imeneyo adzapereka mphoto kwa aliyense mogwirizana ndi makhalidwe ake.+ 28 Ndithu ndikukuuzani kuti pali ena mwa amene aimirira pano amene sadzalawa imfa mʼpangʼono pomwe mpaka choyamba ataona Mwana wa munthu akubwera monga Mfumu.”+
17 Patapita masiku 6, Yesu anatenga Petulo, Yakobo ndi mchimwene wake Yohane nʼkukwera nawo mʼphiri lalitali kwaokhaokha.+ 2 Ndiyeno iwo anaona kuti wasintha maonekedwe ake. Nkhope yake inawala ngati dzuwa ndipo malaya ake akunja anawala* kwambiri.+ 3 Kenako anaona Mose ndi Eliya akukambirana ndi Yesu. 4 Ndiye Petulo anauza Yesu kuti: “Ambuye, zingakhale bwino ife titamakhala pano. Ngati mukufuna, ndimanga matenti atatu pano, imodzi yanu, imodzi ya Mose ndi ina ya Eliya.” 5 Mawu ake adakali mʼkamwa, mtambo wowala kwambiri unawaphimba ndipo panamveka mawu kuchokera mumtambomo akuti: “Uyu ndi Mwana wanga wokondedwa, amene amandisangalatsa kwambiri.+ Muzimumvera.”+ 6 Ophunzirawo atamva zimenezi, anagwada nʼkuwerama mpaka nkhope zawo pansi ndipo anachita mantha kwambiri. 7 Kenako Yesu anawayandikira ndipo anawagwira nʼkunena kuti: “Dzukani, musaope.” 8 Atayangʼana, anaona kuti palibe wina aliyense koma Yesu yekha. 9 Akutsika mʼphirimo, Yesu anawalamula kuti: “Musauze wina aliyense za masomphenya amenewa mpaka Mwana wa munthu ataukitsidwa kwa akufa.”+
10 Koma ophunzirawo anamufunsa kuti: “Nanga nʼchifukwa chiyani alembi amanena kuti Eliya ayenera kubwera choyamba?”+ 11 Iye anayankha kuti: “Inde, Eliya adzabweradi ndipo adzabwezeretsa zinthu zonse.+ 12 Komabe, ine ndikukuuzani kuti Eliya anabwera kale koma iwo sanamuzindikire ndipo anamuchitira zilizonse zimene iwo anafuna.+ Iwo adzazunzanso Mwana wa munthu mwa njira imeneyi.”+ 13 Atatero ophunzirawo anazindikira kuti akunena za Yohane Mʼbatizi.
14 Atafika kufupi ndi gulu la anthu,+ mwamuna wina anamuyandikira ndipo anamugwadira nʼkunena kuti: 15 “Ambuye, muchitire chifundo mwana wanga wamwamuna, chifukwa akudwala matenda akugwa ndipo akuvutika kwambiri. Nthawi zambiri amagwera pamoto ndiponso mʼmadzi.+ 16 Ndinapita naye kwa ophunzira anu koma alephera kumuchiritsa.” 17 Yesu anayankha kuti: “Inu mʼbadwo wopanda chikhulupiriro ndi wopotoka maganizo,+ kodi ndikhala nanube mpaka liti? Ndipitirize kukupirirani mpaka liti? Bwera nayeni kuno.” 18 Ndiyeno Yesu anadzudzula chiwandacho ndipo chinatuluka. Nthawi yomweyo mnyamatayo anachira.+ 19 Kenako ophunzira anapita kwa Yesu ali kwayekha nʼkumufunsa kuti: “Nʼchifukwa chiyani ife tinalephera kutulutsa chiwanda chija?” 20 Iye anawayankha kuti: “Chifukwa cha kuchepa kwa chikhulupiriro chanu. Ndithu ndikukuuzani, ngati mutakhala ndi chikhulupiriro chofanana ndi kanjere ka mpiru kuchepa kwake, mudzatha kuuza phiri ili kuti, ‘Choka pano upite apo,’ ndipo lidzachokadi. Palibe chimene chidzakhale chosatheka kwa inu.”+ 21*——
22 Atasonkhana pamodzi ku Galileya, Yesu anawauza kuti: “Mwana wa munthu adzaperekedwa mʼmanja mwa anthu+ 23 ndipo adzamupha. Koma pa tsiku lachitatu adzaukitsidwa.”+ Atamva zimenezi iwo anamva chisoni kwambiri.
24 Atafika ku Kaperenao, anthu okhometsa msonkho wa madalakima awiri anapita kwa Petulo nʼkumufunsa kuti: “Kodi mphunzitsi wanu amapereka madalakima awiri* a msonkho?”+ 25 Iye anati: “Inde amapereka.” Koma atalowa mʼnyumba, asananene chilichonse, Yesu anamufunsa kuti: “Simoni, ukuganiza bwanji? Kodi mafumu a dziko lapansi amalandira ndalama za ziphaso kapena za msonkho kuchokera kwa ndani? Kuchokera kwa ana awo kapena kwa anthu achilendo?” 26 Atayankha kuti: “Kuchokera kwa anthu achilendo,” Yesu anamuuza kuti: “Ndiye kuti ana sakuyenera kukhoma msonkho. 27 Koma kuti tisawakhumudwitse,+ pita kunyanja, ukaponye mbedza ndipo ukatenge nsomba yoyambirira kuwedza. Ukakaikanula kukamwa kwake, ukapezako khobidi limodzi lasiliva.* Ukalitenge nʼkukhomera msonkho wako ndi wanga.”
18 Pa nthawi imeneyo, ophunzira anabwera pafupi ndi Yesu nʼkumufunsa kuti: “Ndi ndani kwenikweni amene adzakhale wamkulu kwambiri mu Ufumu wakumwamba?”+ 2 Choncho iye anaitana mwana wamngʼono nʼkumuimika pakati pawo. 3 Kenako anawauza kuti: “Ndithu ndikukuuzani, mukapanda kutembenuka*+ nʼkukhala ngati ana aangʼono, simudzalowa mu Ufumu wakumwamba.+ 4 Choncho aliyense amene adzadzichepetse ngati mwana wamngʼonoyu ndi amene adzakhale wamkulu kwambiri mu Ufumu wakumwamba.+ 5 Ndiponso aliyense amene walandira mwana wamngʼono ngati ameneyu mʼdzina langa walandiranso ine. 6 Koma aliyense wokhumudwitsa mmodzi wa tiana iti timene timandikhulupirira, zingamukhalire bwino kwambiri kumumangirira chimwala cha mphero mʼkhosi mwake chimene bulu amayendetsa, nʼkumuponyera mʼnyanja yakuya.+
7 Tsoka kwa dzikoli chifukwa cha zopunthwitsa! Inde sitingachitire mwina, zopunthwitsazo ziyenera kubwera ndithu, koma tsoka kwa munthu wobweretsa chopunthwitsa! 8 Choncho ngati dzanja lako kapena phazi lako limakupunthwitsa, ulidule nʼkulitaya kutali.+ Ndi bwino kuti ukapeze moyo ulibe chiwalo chimodzi kapena uli wolumala kusiyana nʼkuti uponyedwe mʼmoto wosatha uli ndi manja onse awiri kapena mapazi onse awiri.+ 9 Komanso ngati diso lako limakuchimwitsa* ulikolowole nʼkulitaya kutali. Ndi bwino kuti ukapeze moyo uli ndi diso limodzi kusiyana nʼkuti uponyedwe mu Gehena* wamoto uli ndi maso onse awiri.+ 10 Samalani anthu inu kuti musanyoze mmodzi wa tianati, chifukwa ndikukutsimikizirani kuti angelo awo kumwamba amaona nkhope ya Atate wanga wakumwamba nthawi zonse.+ 11*——
12 Mukuganiza bwanji? Ngati munthu ali ndi nkhosa 100 ndipo imodzi mwa nkhosazo nʼkusochera,+ kodi sangasiye nkhosa 99 zija mʼphiri nʼkupita kukafunafuna yosocherayo?+ 13 Akaipeza, ndithu ndikukuuzani, amasangalala kwambiri ndi nkhosa imeneyo kusiyana ndi nkhosa 99 zimene sizinasochere zija. 14 Mofanana ndi zimenezi, Atate wanga* wakumwamba sakufuna kuti ngakhale mmodzi wa tiana timeneti awonongeke.+
15 Komanso ngati mʼbale wako wachimwa, upite kukamufotokozera zimene walakwitsazo* panokha, iwe ndi iyeyo.+ Ngati wakumvera, ndiye kuti wabweza mʼbale wakoyo.+ 16 Koma akapanda kukumvera, upiteko ndi munthu wina mmodzi kapena awiri, kuti nkhani yonse ikatsimikizike ndi umboni wa mboni* ziwiri kapena zitatu.+ 17 Amenewanso akapanda kuwamvera, uuze mpingo. Ndipo mpingowo akapandanso kuumvera, kwa iwe akhale ngati munthu wochokera kumtundu wina+ komanso ngati wokhometsa msonkho.+
18 Ndithu ndikukuuzani, zilizonse zimene mudzamange padziko lapansi zidzakhala zoti zamangidwa kale kumwamba. Ndipo zilizonse zimene mudzamasule padziko lapansi zidzakhala zoti zamasulidwa kale kumwamba. 19 Ndiponso ndikukuuzani kuti, ngati awiri mwa inu padziko lapansi pano mutagwirizana kuti mupemphe chinthu chilichonse chofunika, Atate wanga wakumwamba adzakuchitirani.+ 20 Chifukwa kulikonse kumene awiri kapena atatu asonkhana mʼdzina langa,+ ine ndidzakhala pakati pawo.”
21 Kenako Petulo anabwera nʼkumufunsa kuti: “Ambuye, kodi mʼbale wanga ndizimukhululukira kangati akamandichimwira? Mpaka maulendo 7 kodi?” 22 Yesu anamuyankha kuti: “Ndikukuuza kuti, osati maulendo 7 okha ayi, koma mpaka maulendo 77.+
23 Nʼchifukwa chake Ufumu wakumwamba tingauyerekezere ndi mfumu imene inkafuna kuti akapolo ake abweze ngongole. 24 Mfumuyo itayamba kulandira ngongolezo, atumiki ake anabweretsa munthu amene anali ndi ngongole ya matalente 10,000.* 25 Koma chifukwa choti sakanakwanitsa kubweza ngongoleyo, mbuye wake analamula kuti mwamuna ameneyu, mkazi wake, ana ake komanso zonse zimene anali nazo zigulitsidwe nʼkumubwezera ndalama zake.+ 26 Ndiyeno kapoloyu anagwada pansi nʼkumuweramira ndipo ananena kuti, ‘Ndilezereni mtima chonde, ndidzakubwezerani zonse.’ 27 Mbuyeyo anamva chisoni ndi zimenezi ndipo anamusiya kapoloyo nʼkumukhululukira ngongole yake ija.+ 28 Koma kapolo ameneyu atatuluka anakumana ndi kapolo mnzake amene anali ndi ngongole yake yokwana madinari 100.* Choncho anamugwira nʼkuyamba kumukanyanga pakhosi, akunena kuti, ‘Bweza ngongole ija mwamsanga.’ 29 Kapolo mnzakeyo anagwada pansi nʼkuyamba kumudandaulira kuti, ‘Ndilezereni mtima chonde, ndidzakubwezerani.’ 30 Koma iye sanalole ndipo anapita naye kundende kuti akamutsekere mpaka atamaliza kubweza ngongoleyo. 31 Akapolo anzake ataona zimene zinachitikazo, anamva chisoni kwambiri ndipo anapita kwa mbuye wawo nʼkukamufotokozera zonse zimene zinachitika. 32 Ndiyeno mbuye wakeyo anamuitanitsa nʼkumuuza kuti: ‘Kapolo woipa iwe, ine ndakukhululukira ngongole yonse ija utandidandaulira. 33 Kodi sukanamuchitira chifundo kapolo mnzako, ngati mmene ine ndachitira kwa iwe?’+ 34 Choncho mbuye wakeyo anakwiya kwambiri ndipo anapita naye kwa oyangʼanira ndende kuti amutsekere mpaka atamaliza kubweza ngongole yonse ija. 35 Atate wanga wakumwamba adzakuchitiraninso zofanana ndi zimenezi+ ngati aliyense wa inu sakhululukira mʼbale wake ndi mtima wonse.”+
19 Yesu atamaliza kulankhula zinthu zimenezi, anachoka ku Galileya nʼkupita kumalire a Yudeya kutsidya lina la Yorodano.+ 2 Gulu lalikulu la anthu linamutsatira kumeneko ndipo iye anawachiritsa.
3 Ndiyeno Afarisi anabwera kwa iye nʼcholinga chodzamuyesa ndipo anamufunsa kuti: “Kodi mwamuna ali ndi ufulu wothetsa banja ndi mkazi wake pa chifukwa chilichonse?”+ 4 Yesu anayankha kuti: “Kodi simunawerenge kuti amene analenga anthu pachiyambi anawalenga mwamuna ndi mkazi+ 5 nʼkunena kuti: ‘Chifukwa cha zimenezi mwamuna adzasiya bambo ake ndi mayi ake nʼkudziphatika kwa mkazi wake ndipo awiriwo adzakhala thupi limodziʼ?+ 6 Moti sakhalanso kuti ndi awiri, koma thupi limodzi. Choncho chimene Mulungu wachimanga pamodzi,* munthu asachilekanitse.”+ 7 Iwo anamufunsa kuti: “Nanga nʼchifukwa chiyani Mose analamula kuti mwamuna azipereka kalata yothetsera ukwati kwa mkazi nʼkumusiya?”+ 8 Iye anawayankha kuti: “Chifukwa cha kuuma mtima kwanu, Mose anakulolezani kuti muzithetsa ukwati,+ koma kuyambira pachiyambi sizinali choncho.+ 9 Ine ndikukuuzani kuti aliyense amene wasiya mkazi wake nʼkukwatira wina wachita chigololo, kupatulapo ngati wamusiya chifukwa cha chiwerewere.”*+
10 Kenako ophunzira ake ananena kuti: “Ngati zili choncho kwa munthu ndi mkazi wake, ndiyetu ndi bwino osakwatira.” 11 Iye anawauza kuti: “Si onse amene angathe kuchita zimenezi, koma okhawo amene ali ndi mphatso.+ 12 Chifukwa ena sakwatira chifukwa chakuti anabadwa choncho ndipo ena chifukwa chakuti anafulidwa ndi anthu. Koma pali ena amene safuna kukwatira chifukwa cha Ufumu wakumwamba. Amene angathe kuchita zimenezi achite.”+
13 Kenako anthu anamubweretsera ana aangʼono kuti awaike manja nʼkuwapempherera, koma ophunzirawo anawakalipira.+ 14 Koma Yesu anawauza kuti: “Asiyeni anawo ndipo musawaletse kuti abwere kwa ine, chifukwa Ufumu wakumwamba ndi wa anthu ngati amenewa.”+ 15 Ndiyeno anaika manja ake pa anawo kenako anachoka kumeneko.
16 Tsopano munthu wina anabwera kwa iye nʼkumufunsa kuti: “Mphunzitsi, kodi ndi zinthu zabwino ziti zimene ndikuyenera kuchita kuti ndikapeze moyo wosatha?”+ 17 Iye anamuyankha kuti: “Nʼchifukwa chiyani ukundifunsa zokhudza zinthu zabwino? Pali mmodzi yekha amene ndi wabwino.+ Choncho ngati ukufuna kukapeza moyo, uzisunga malamulo nthawi zonse.”+ 18 Iye anafunsa kuti: “Malamulo ake ati?” Yesu anayankha kuti: “Musaphe munthu,*+ musachite chigololo,+ musabe,+ musapereke umboni wabodza.+ 19 Muzilemekeza bambo anu ndi mayi anu,+ komanso lakuti, Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.”+ 20 Mnyamatayo anayankha Yesu kuti: “Ndakhala ndikutsatira zonsezi, nʼchiyaninso china chimene ndikuyenera kuchita?” 21 Yesu anamuuza kuti: “Ngati ukufuna kukhala wangwiro,* pita ukagulitse katundu wako yense ndipo ndalama zake ukapatse osauka. Ukatero udzakhala ndi chuma kumwamba,+ ndiyeno ubwere udzakhale wotsatira wanga.”+ 22 Mnyamatayo atamva zimenezi anachoka ali ndi chisoni, chifukwa anali ndi katundu wambiri.+ 23 Ndiyeno Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Ndithu ndikukuuzani, zidzakhala zovuta kuti munthu wolemera adzalowe mu Ufumu wakumwamba.+ 24 Ndiponso ndikukuuzani kuti, nʼzosavuta kuti ngamila ilowe pakabowo ka singano kusiyana nʼkuti munthu wolemera alowe mu Ufumu wa Mulungu.”+
25 Ophunzirawo atamva zimenezi, anadabwa kwambiri ndipo anafunsa kuti: “Ndiye angapulumuke ndi ndani?”+ 26 Yesu anawayangʼanitsitsa nʼkuwauza kuti: “Kwa anthu zimenezi nʼzosatheka, koma zinthu zonse nʼzotheka kwa Mulungu.”+
27 Kenako Petulo ananena kuti: “Taonani! Ife tasiya zinthu zonse nʼkukutsatirani, ndiye kodi tidzapeza chiyani?”+ 28 Yesu anawauza kuti: “Ndithu ndikukuuzani, pa nthawi ya kulenganso zinthu, Mwana wa munthu adzakhala pampando wake wachifumu waulemerero, inu amene mwakhala mukunditsatira mudzakhalanso mʼmipando yachifumu 12, nʼkumaweruza mafuko 12 a Isiraeli.+ 29 Aliyense amene wasiya nyumba, azichimwene, azichemwali, abambo, amayi, ana kapena minda chifukwa cha dzina langa adzalandira zochuluka kuwirikiza maulendo 100 kuposa zimenezi ndiponso adzapeza moyo wosatha.+
30 Koma ambiri amene ali oyamba adzakhala omaliza ndipo omaliza adzakhala oyamba.”+
20 “Ufumu wakumwamba uli ngati munthu amene anali ndi munda wa mpesa, amene analawirira mʼmawa kwambiri kukafuna anthu aganyu kuti akagwire ntchito mʼmunda wake wa mpesa.+ 2 Aganyu amenewa atagwirizana nawo kuti aziwapatsa ndalama ya dinari* imodzi pa tsiku, anawatumiza kumunda wake wa mpesa. 3 Cha mʼma 9 koloko mʼmawa* anapitanso kukafuna anthu ena, ndipo anaona ena atangoimaima pamsika alibe chochita. 4 Amenewonso anawauza kuti, ‘Inunso kagwireni ntchito mʼmunda wa mpesa. Ndidzakupatsani malipiro oyenerera.’ 5 Choncho iwo anapita. Cha mʼma 12 koloko ndi 3 koloko masana,* mwinimunda uja anapitanso kukachita chimodzimodzi. 6 Pamapeto pake, cha mʼma 5 koloko madzulo* anapitanso ndipo anakapeza ena atangoimaima. Iye anawafunsa kuti, ‘Nʼchifukwa chiyani mwangoimaima pano tsiku lonse osagwira ntchito?’ 7 Iwo anamuyankha kuti, ‘Chifukwa palibe amene watilemba ganyu.’ Iye anawauza kuti, ‘Inunso pitani mukagwire ntchito kumunda wanga wa mpesa.’
8 Madzulowo, mwiniwake wa munda wa mpesa uja anauza kapitawo wake kuti, ‘Itana antchito aja uwapatse malipiro awo,+ kuyambira omalizira, kutsiriza ndi oyambirira.’ 9 Anthu amene anayamba ntchito 5 koloko aja atafika, aliyense analandira dinari* imodzi. 10 Choncho oyambirira aja atafika, anaganiza kuti alandira zambiri, koma nawonso malipiro amene analandira anali dinari* imodzi. 11 Atalandira, anayamba kudandaulira mwiniwake wa munda wa mpesa uja 12 kuti, ‘Omalizirawa agwira ntchito ola limodzi lokha, koma mwawapatsa malipiro ofanana ndi ife amene tagwira ntchito yakalavulagaga tsiku lonse padzuwa lotentha!’ 13 Koma poyankha kwa mmodzi wa iwo, mwinimundayo anati, ‘Bwanawe, sindinakulakwire. Tinapangana malipiro a dinari* imodzi, si choncho?+ 14 Ingolandira malipiro ako uzipita. Ndikufuna kupatsa womalizirayu malipiro ofanana ndi amene ndapereka kwa iwe. 15 Kodi ndilibe ufulu wochita zimene ndikufuna ndi zinthu zanga? Kapena kodi diso lako lachita njiru* chifukwa chakuti ndine wabwino?’*+ 16 Choncho omalizira adzakhala oyambirira ndipo oyambirira adzakhala omalizira.”+
17 Ali panjira yopita ku Yerusalemu, Yesu anatengera pambali ophunzira ake 12 aja nʼkuwauza kuti:+ 18 “Tsopano tikupita ku Yerusalemu ndipo Mwana wa munthu akaperekedwa kwa ansembe aakulu ndi alembi. Iwo akamuweruza kuti aphedwe+ 19 ndipo akamupereka kwa anthu a mitundu ina kuti amuchitire chipongwe, kumukwapula ndi kumupachika pamtengo+ ndipo pa tsiku lachitatu adzaukitsidwa.”+
20 Kenako mkazi wa Zebedayo+ anafika kwa Yesu ndi ana ake aamuna ndipo anamugwadira nʼkumupempha kanthu kena.+ 21 Iye anafunsa mayiyo kuti: “Mukufuna chiyani?” Mayiyo anayankha kuti: “Lonjezani kuti ana anga aamuna awiriwa, mmodzi adzakhale kudzanja lanu lamanja, wina kudzanja lanu lamanzere mu Ufumu wanu.”+ 22 Yesu anayankha kuti: “Simukudziwa chimene mukupempha. Kodi mungamwe zimene ine ndatsala pangʼono kumwa?”+ Iwo anayankha kuti: “Inde tingamwe.” 23 Iye anawauza kuti: “Inde mudzamwadi zimene ndatsala pangʼono kumwa.+ Koma si ine woyenera kusankha amene adzakhale kudzanja langa lamanja kapena lamanzere. Atate wanga adzapereka mwayi umenewo kwa amene anawakonzera.”+
24 Ophunzira 10 ena aja atamva zimenezi, anakwiya kwambiri ndi amuna awiri apachibalewo.+ 25 Koma Yesu anawaitana nʼkuwauza kuti: “Inu mukudziwa kuti olamulira a anthu a mitundu ina amapondereza anthu awo ndipo akuluakulu amasonyeza mphamvu zawo pa iwo.+ 26 Sizikuyenera kukhala choncho pakati panu.+ Koma aliyense amene akufuna kuti akhale wamkulu pakati panu akuyenera kukhala mtumiki wanu+ 27 ndipo amene akufuna kuti akhale woyamba pakati panu akuyenera kukhala kapolo wanu.+ 28 Izi zikufanana ndi zimene Mwana wa munthu anachita. Iye sanabwere kudzatumikiridwa koma kudzatumikira+ ndi kudzapereka moyo wake dipo* kuti awombole anthu ambiri.”+
29 Pamene iwo ankatuluka mu Yeriko, gulu lalikulu la anthu linamutsatira. 30 Ndiyeno amuna awiri amene anali ndi vuto losaona anakhala pansi mʼmphepete mwa msewu ndipo atamva kuti Yesu akudutsa, anafuula kuti: “Ambuye, Mwana wa Davide, tichitireni chifundo!”+ 31 Ndiye gulu la anthulo linawakalipira nʼkuwauza kuti akhale chete. Koma mʼpamene iwo anafuula kwambiri kuti: “Ambuye, Mwana wa Davide, tichitireni chifundo!” 32 Choncho Yesu anaima, ndipo anawaitana nʼkuwafunsa kuti: “Mukufuna kuti ndikuchitireni chiyani?” 33 Iwo anamuyankha kuti: “Ambuye, tithandizeni kuti tiyambe kuona.” 34 Atagwidwa ndi chifundo, Yesu anagwira maso awo.+ Nthawi yomweyo anthu amene anali ndi vuto losaonawo anayamba kuona ndipo anamutsatira.
21 Atayandikira ku Yerusalemu nʼkufika ku Betefage paphiri la Maolivi, Yesu anatuma ophunzira awiri.+ 2 Iye anawauza kuti: “Pitani mʼmudzi umene mukuuonawo. Kumeneko mukapeza bulu atamumangirira limodzi ndi mwana wake wamphongo. Mukawamasule nʼkuwabweretsa kwa ine. 3 Ngati wina atakufunsani chilichonse, mukanene kuti, ‘Ambuye akuwafuna.’ Ndipo nthawi yomweyo akawatumiza kuno.”
4 Izi zinachitikadi kuti zimene Mulungu ananena kudzera mwa mneneri zikwaniritsidwe, zakuti: 5 “Uzani mwana wamkazi wa Ziyoni* kuti: ‘Taona! Mfumu yako ikubwera kwa iwe.+ Ndi yofatsa+ ndipo yakwera bulu, yakwera mwana wamphongo wa bulu, mwana wa nyama yonyamula katundu.’”+
6 Choncho ophunzirawo ananyamuka nʼkukachita zimene Yesu anawauza.+ 7 Iwo anabweretsa bulu uja limodzi ndi mwana wake wamphongo. Kenako anayala malaya awo akunja pa abuluwo ndipo iye anakwera pamwana wa buluyo.+ 8 Anthu ambiri amene anali pamenepo anayala malaya awo akunja mumsewu+ ndipo ena ankadula nthambi za mitengo nʼkuziyala mumsewu. 9 Komanso gulu la anthu limene linali patsogolo pake ndi mʼmbuyo mwake linkafuula kuti: “Mʼpulumutseni Mwana wa Davide!+ Wodalitsidwa ndi amene akubwera mʼdzina la Yehova!*+ Mʼpulumutseni kumwambamwambako!”+
10 Atalowa mu Yerusalemu, mzinda wonse unagwedezeka ndipo ena ankafunsa kuti: “Kodi ameneyu ndi ndani?” 11 Gulu la anthulo linkayankha kuti: “Ameneyu ndi mneneri Yesu,+ wochokera ku Nazareti, ku Galileya!”
12 Kenako Yesu analowa mʼkachisi nʼkuthamangitsa anthu onse amene ankagulitsa ndi kugula zinthu mʼkachisimo, ndipo anagubuduza matebulo a anthu amene ankasintha ndalama komanso mabenchi a anthu amene ankagulitsa nkhunda.+ 13 Iye anawauza kuti: “Malemba amati, ‘Nyumba yanga idzatchedwa nyumba yopemphereramo,’+ koma inu mukuisandutsa phanga la achifwamba.”+ 14 Kenako anthu amene anali ndi vuto losaona komanso olumala anabwera kwa iye mʼkachisimo ndipo anawachiritsa.
15 Ansembe aakulu ndi alembi ataona zodabwitsa zimene anachitazo komanso anyamata amene ankafuula mʼkachisimo kuti, “Mʼpulumutseni Mwana wa Davide!”+ anakwiya kwambiri+ 16 ndipo anamufunsa kuti: “Kodi ukumva zimene anthu akunenazi?” Yesu anayankha kuti: “Inde. Kodi simunawerenge zimenezi kuti, ‘Mwachititsa kuti mʼkamwa mwa ana ndi mwa makanda mutuluke mawu otamandaʼ?”+ 17 Kenako iye anawasiya nʼkutuluka mumzindawo kupita ku Betaniya ndipo anagona kumeneko.+
18 Akubwerera kumzinda uja mʼmawa kwambiri, anamva njala.+ 19 Kenako anaona mtengo wamkuyu mʼmbali mwa msewu ndipo atapita pomwepo, sanapezemo chilichonse koma masamba okhaokha.+ Choncho anauza mtengowo kuti: “Kuyambira lero sudzaberekanso chipatso chilichonse.”+ Ndipo mkuyuwo unafota nthawi yomweyo. 20 Ophunzira aja ataona zimenezi, anadabwa nʼkunena kuti: “Zatheka bwanji kuti mkuyuwu ufote nthawi yomweyi?”+ 21 Poyankha Yesu anawauza kuti: “Ndithu ndikukuuzani, ngati mutakhala ndi chikhulupiriro ndipo simukukayikira, mudzatha kuchita zimene ndachitira mkuyu umenewu. Komanso kuposa pamenepa, mudzatha kuuza phiri ili kuti, ‘Nyamuka pano ukadziponye mʼnyanja,’ ndipo zidzachitikadi.+ 22 Zinthu zonse zimene mudzapemphe mʼmapemphero anu, mudzalandira ngati muli ndi chikhulupiriro.”+
23 Yesu atalowa mʼkachisi nʼkumaphunzitsa, ansembe aakulu ndiponso akulu anabwera kwa iye nʼkumufunsa kuti: “Kodi muli ndi ulamuliro wochitira zinthu zimenezi? Ndipo ndi ndani amene anakupatsani ulamuliro umenewu?”+ 24 Yesu anawayankha kuti: “Inenso ndikufunsani chinthu chimodzi. Mukandiyankha chinthu chimenecho, inenso ndikuuzani amene anandipatsa ulamuliro umene ndimachitira zimenezi: 25 Kodi ubatizo umene Yohane ankachita unachokera kuti? Kumwamba kapena kwa anthu?” Koma iwo anayamba kukambirana kuti: “Tikanena kuti, ‘Unachokera kumwamba,’ atifunsa kuti, ‘Nanga nʼchifukwa chiyani simunamukhulupirire?’+ 26 Komanso sitinganene kuti, ‘Unachokera kwa anthu,’ chifukwa tikuopa gulu la anthuli, popeza onsewa amakhulupirira kuti Yohane anali mneneri.” 27 Choncho iwo anayankha Yesu kuti: “Sitikudziwa.” Nayenso anawauza kuti: “Inenso sindikuuzani amene anandipatsa ulamuliro umene ndimachitira zimenezi.
28 Kodi mukuganiza bwanji? Munthu wina anali ndi ana awiri. Ndipo anapita kwa mwana woyamba nʼkumuuza kuti, ‘Mwana wanga, lero upite kukagwira ntchito mʼmunda wa mpesa.’ 29 Iye anayankha kuti, ‘Sindipita,’ koma kenako anasintha maganizo nʼkupita. 30 Kenako anapita kwa mwana wachiwiri nʼkumuuzanso chimodzimodzi. Iye anayankha kuti, ‘Ndipita bambo,’ koma sanapite. 31 Ndi ndani mwa ana awiriwa amene anachita zimene bambo ake ankafuna?” Iwo anayankha kuti: “Woyambayo.” Yesu anawauza kuti: “Ndithu ndikukuuzani kuti okhometsa msonkho ndiponso mahule akukusiyani mʼmbuyo nʼkukalowa mu Ufumu wa Mulungu. 32 Chifukwa Yohane anabwera kwa inu kudzakuphunzitsani njira yachilungamo, koma inu simunamukhulupirire. Koma okhometsa msonkho ndi mahule anamukhulupirira.+ Ngakhale kuti inu munaona zimenezi, simunasinthe maganizo anu nʼkuyamba kumukhulupirira.
33 Mvetserani fanizo lina: Panali munthu wina yemwe analima munda wa mpesa+ nʼkumanga mpanda kuzungulira mundawo. Komanso anakumba dzenje loponderamo mphesa nʼkumanga nsanja.+ Atatero anausiya mʼmanja mwa alimi nʼkupita kudziko lina.+ 34 Nyengo ya zipatso itafika, anatumiza akapolo ake kwa alimiwo kuti akatenge zipatso zake. 35 Koma alimiwo anagwira akapolo ake aja ndipo mmodzi anamumenya, wina anamupha, wina anamugenda ndi miyala.+ 36 Anatumizanso akapolo ena ambiri kuposa oyamba aja, koma amenewanso anawachitira zomwezo.+ 37 Pamapeto pake anawatumizira mwana wake, nʼkunena kuti, ‘Mwana wanga yekhayu akamulemekeza.’ 38 Alimiwo ataona mwanayo anayamba kukambirana kuti, ‘Eyaa! uyu ndi amene adzalandire cholowa.+ Bwerani, tiyeni timuphe nʼkutenga cholowa chakecho!’ 39 Choncho anamugwira nʼkumutulutsa mʼmunda wa mpesawo ndipo anamupha.+ 40 Ndiye kodi mwiniwake wa munda wa mpesa uja akadzabwera, adzachita nawo chiyani alimiwo?” 41 Iwo anayankha kuti: “Chifukwa chakuti ndi oipa, adzawawononga koopsa ndipo munda wa mpesawo adzaupereka kwa alimi ena, amene angamupatse zipatso mʼnyengo yake.”
42 Ndiyeno Yesu anawauza kuti: “Paja Malemba amanena kuti, ‘Mwala umene omanga nyumba anaukana wakhala mwala wapakona wofunika kwambiri.*+ Umenewu wachokera kwa Yehova* ndipo ndi wodabwitsa mʼmaso mwathu.+ Kodi simunawerenge zimeneziʼ? 43 Nʼchifukwa chake ndikukuuzani kuti, Ufumu wa Mulungu udzachotsedwa kwa inu nʼkuperekedwa ku mtundu wobereka zipatso zake. 44 Komanso munthu amene adzagwere pamwala umenewu adzaphwanyika.+ Ndipo aliyense amene mwalawo udzamugwere, adzanyenyeka.”+
45 Ansembe aakulu ndi Afarisi atamva mafanizo akewa, anazindikira kuti akunena za iwowo.+ 46 Komabe ngakhale kuti ankafuna kumugwira,* ankaopa gulu la anthu chifukwa anthuwo ankakhulupirira kuti iye ndi mneneri.+
22 Yesu anawauzanso mafanizo ena kuti: 2 “Ufumu wakumwamba tingauyerekezere ndi mfumu imene inakonzera mwana wake wamwamuna phwando la ukwati.+ 3 Ndipo inatuma akapolo ake kuti akaitane anthu oitanidwa kuphwando laukwati, koma anthuwo sanafune kubwera.+ 4 Kenako inatumanso akapolo ena kuti, ‘Kauzeni oitanidwawo kuti: “Ine ndakonza chakudya chamasana, ngʼombe zanga zamphongo komanso nyama zanga zonenepa zaphedwa, ndipo zinthu zonse zakonzedwa kale. Bwerani kuphwando laukwati.”’ 5 Koma anthuwo ananyalanyaza nʼkuchoka. Wina anapita kumunda wake ndipo wina anapita kumalonda ake.+ 6 Koma enawo anagwira akapolo akewo ndipo anawachitira chipongwe nʼkuwapha.
7 Zitatero mfumu ija inakwiya kwambiri ndipo inatumiza asilikali ake kukapha anthu amene anapha akapolo akewo nʼkuwotcha mzinda wawo.+ 8 Kenako anauza akapolo ake kuti, ‘Phwando laukwati ndiye lakonzedwa, koma oitanidwa aja anali osayenera.+ 9 Choncho pitani mʼmisewu yotulukira mumzinda ndipo aliyense amene mukamupeze, mukamuitane kuti abwere kuphwando laukwatili.’+ 10 Ndiyeno akapolowo anapita mʼmisewu ndipo anasonkhanitsa onse amene anawapeza, oipa ndi abwino omwe. Ndipo chipinda chodyeramo phwando laukwati chinadzaza ndi anthu amene ankadya chakudya.
11 Mfumu ija italowa kukayendera alendowo, inaona munthu wina mmenemo amene sanavale chovala chaukwati. 12 Choncho inamufunsa kuti, ‘Bwanawe! Walowa bwanji muno usanavale chovala cha ukwati?’ Iye anasowa chonena. 13 Kenako mfumuyo inauza atumiki ake kuti, ‘Mʼmangeni manja ndi miyendo ndipo mumuponye kunja kumdima. Kumeneko akalira ndi kukukuta mano.’
14 Chifukwa oitanidwa ndi ambiri, koma osankhidwa ndi owerengeka.”
15 Kenako Afarisi anachoka nʼkukapangana kuti amupezere zifukwa pa zimene angalankhule.+ 16 Choncho anamutumizira ophunzira awo, limodzi ndi anthu amene ankatsatira Herode,+ ndipo iwo ananena kuti: “Mphunzitsi, tikudziwa kuti inu mumanena zoona ndipo mumaphunzitsa njira ya Mulungu mʼchoonadi, ndiponso simuchita zinthu pongofuna kusangalatsa munthu, chifukwa simuyangʼana maonekedwe a anthu. 17 Ndiye tatiuzani, mukuganiza bwanji? Kodi nʼzololeka* kupereka msonkho kwa Kaisara kapena ayi?” 18 Koma Yesu anadziwa kuipa mtima kwawo ndipo ananena kuti: “Anthu achinyengo inu! Bwanji mukundiyesa? 19 Ndionetseni khobidi la msonkho.” Iwo anamubweretsera khobidi limodzi la dinari.* 20 Ndiyeno anawafunsa kuti: “Kodi nkhope iyi komanso mawu akewa nʼzandani?” 21 Iwo anayankha kuti: “Ndi za Kaisara.” Choncho iye anawauza kuti: “Ndiye perekani zinthu za Kaisara kwa Kaisara, koma za Mulungu kwa Mulungu.”+ 22 Atamva zimenezi, anadabwa ndipo anangochokapo nʼkumusiya.
23 Pa tsiku limenelo Asaduki amene amanena kuti akufa sadzaukitsidwa,+ anabwera nʼkumufunsa kuti:+ 24 “Mphunzitsi, Mose ananena kuti: ‘Ngati mwamuna wamwalira asanabereke ana, mchimwene wake akuyenera kukwatira mkazi wamasiyeyo nʼkuberekera mchimwene wake uja ana.’+ 25 Tsopano panali amuna 7 apachibale. Woyamba anakwatira kenako nʼkumwalira. Koma popeza kuti analibe ana, mkaziyo anakwatiwa ndi mchimwene wa mwamuna wake uja. 26 Zinachitika chimodzimodzi kwa wachiwiri ndi wachitatu, mpaka kwa onse 7 aja. 27 Pamapeto pake mkazi uja anamwaliranso. 28 Kodi pamenepa, akufa akadzaukitsidwa mkazi ameneyu adzakhala wa ndani? Popeza onse 7 anamukwatira.”
29 Koma Yesu anawayankha kuti: “Mukulakwitsa chifukwa simudziwa Malemba kapena mphamvu ya Mulungu.+ 30 Chifukwa akufa akadzaukitsidwa, amuna sadzakwatira ndipo akazi sadzakwatiwa, koma adzakhala ngati angelo akumwamba.+ 31 Kunena za kuuka kwa akufa, kodi simunawerenge zimene Mulungu ananena kwa inu kuti: 32 ‘Ine ndine Mulungu wa Abulahamu, Mulungu wa Isaki ndi Mulungu wa Yakoboʼ?+ Iye ndi Mulungu wa anthu amoyo, osati akufa.”+ 33 Gulu la anthulo litamva zimenezo, linadabwa ndi zimene ankaphunzitsa.+
34 Afarisi atamva kuti Yesu anawasowetsa chonena Asaduki, anasonkhana monga gulu limodzi. 35 Ndipo mmodzi wa iwo, amene ankadziwa Chilamulo, anamuyesa pomufunsa kuti: 36 “Mphunzitsi, kodi lamulo lalikulu kwambiri mʼChilamulo ndi liti?”+ 37 Iye anamuyankha kuti: “‘Muzikonda Yehova* Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, moyo wanu wonse ndi maganizo anu onse.’+ 38 Limeneli ndi lamulo lalikulu kwambiri komanso loyamba. 39 Lachiwiri lofanana nalo ndi ili: ‘Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.’+ 40 Chilamulo chonse chagona pa malamulo awiri amenewa, kuphatikizaponso zimene aneneri analemba.”+
41 Tsopano Afarisi aja atasonkhana pamodzi, Yesu anawafunsa kuti:+ 42 “Mukuganiza bwanji za Khristu? Kodi ndi mwana wa ndani?” Iwo anayankha kuti: “Ndi mwana wa Davide.”+ 43 Iye anawafunsanso kuti: “Nanga nʼchifukwa chiyani mouziridwa ndi mzimu,+ Davide anamutchula kuti Ambuye, pamene ananena kuti, 44 ‘Yehova* anauza Ambuye wanga kuti: “Khala kudzanja langa lamanja mpaka nditaika adani ako pansi pa mapazi ako”’?+ 45 Ndiye ngati Davide anamutchula kuti Ambuye, zikutheka bwanji kuti akhale mwana wake?”+ 46 Panalibe ngakhale mmodzi amene anatha kumuyankha, ndipo kuchokera tsiku limenelo palibe amene analimbanso mtima kumufunsa mafunso.
23 Kenako Yesu anauza gulu la anthu ndi ophunzira ake kuti: 2 “Alembi ndi Afarisi adzikhazika pampando wa Mose. 3 Choncho muzichita ndi kutsatira zinthu zonse zimene angakuuzeni, koma musamachite zimene iwo amachita, chifukwa iwo amangonena koma sachita zimene amanenazo.+ 4 Iwo amamanga akatundu olemera nʼkusenzetsa anthu pamapewa,+ koma eni akewo safuna kusuntha akatunduwo ndi chala chawo.+ 5 Zonse zimene amachita, amazichita kuti anthu awaone.+ Iwo amakulitsa timapukusi tokhala ndi malemba timene amavala monga zodzitetezera,+ ndipo amatalikitsanso ulusi wopota wa mʼmphepete mwa zovala zawo.+ 6 Amakonda malo olemekezeka kwambiri pachakudya chamadzulo ndi mipando yakutsogolo* mʼmasunagoge.+ 7 Amakondanso kupatsidwa moni mʼmisika komanso kuti anthu aziwatchula kuti Rabi.* 8 Koma inu musamatchulidwe kuti Rabi, chifukwa Mphunzitsi+ wanu ndi mmodzi yekha, ndipo nonsenu ndinu abale. 9 Komanso musamatchule aliyense kuti atate wanu padziko lapansi pano, chifukwa Atate+ wanu ndi mmodzi Yekhayo, amene amakhala kumwamba. 10 Musamatchulidwenso kuti atsogoleri, chifukwa Mtsogoleri wanu ndi mmodzi, Khristu. 11 Koma wamkulu kwambiri pakati panu akhale mtumiki wanu.+ 12 Aliyense amene amadzikweza adzatsitsidwa,+ koma aliyense amene amadzichepetsa adzakwezedwa.+
13 Tsoka kwa inu alembi ndi Afarisi, anthu achinyengo inu! Chifukwa mukutseka Ufumu wakumwamba kuti anthu asalowemo. Popeza inuyo simukulowamo, mukuletsa amene akufuna kulowamo kuti asalowe.+ 14*——
15 Tsoka kwa inu alembi ndi Afarisi, anthu achinyengo inu!+ Chifukwa mumawoloka nyanja komanso kuyenda mitunda italiitali kuti mukatembenuze munthu mmodzi. Koma akatembenuka mumamupangitsa kuti akhale woyenera kuponyedwa mʼGehena* kuposa inuyo.
16 Tsoka kwa inu atsogoleri akhungu,+ amene mumati, ‘Ngati munthu watchula kachisi polumbira, palibe kanthu, koma ngati munthu watchula golide wa mʼkachisi, akuyenera kusunga lumbiro lake.’+ 17 Anthu opusa komanso akhungu inu! Chofunika kwambiri ndi chiti, golide kapena kachisi amene wayeretsa golideyo? 18 Komanso mumati, ‘Ngati munthu watchula guwa lansembe polumbira, palibe kanthu, koma ngati munthu watchula mphatso imene ili paguwapo polumbira, asunge lumbiro lake.’ 19 Anthu akhungu inu! Chofunika kwambiri ndi chiti, mphatso kapena guwa lansembe limene limayeretsa mphatsoyo? 20 Choncho amene watchula guwa lansembe polumbira, walumbirira guwalo ndi zinthu zonse zimene zili pamenepo, 21 ndipo amene watchula kachisi polumbira, walumbirira kachisiyo komanso Mulungu amene amakhala mmenemo.+ 22 Ndipo aliyense amene watchula kumwamba polumbira, walumbirira mpando wachifumu wa Mulungu komanso Mulungu amene wakhala pampandowo.
23 Tsoka kwa inu alembi ndi Afarisi, anthu achinyengo inu! Chifukwa mumapereka chakhumi cha timbewu ta minti, dilili ndi chitowe,+ koma mumanyalanyaza zinthu zofunika za mʼChilamulo, zomwe ndi chilungamo,+ chifundo+ ndi kukhulupirika. Kupereka zinthu zimenezi nʼkofunika ndithu, koma osanyalanyaza zinthu zinazo.+ 24 Atsogoleri akhungu inu,+ amene mumasefa zakumwa zanu kuti muchotsemo kanyerere+ koma mumameza ngamila.+
25 Tsoka kwa inu alembi ndi Afarisi, anthu achinyengo inu! Chifukwa muli ngati kapu ndi mbale zimene zatsukidwa kunja kokha+ koma mkati mwake muli mwakuda. Mkati mwa mitima yanu mwadzaza dyera*+ ndi kusadziletsa.+ 26 Mfarisi wakhungu iwe, yeretsa mkati mwa kapu ndi mbale choyamba, kuti kunja kwakenso kukhale koyera.
27 Tsoka kwa inu alembi ndi Afarisi, anthu achinyengo inu!+ Chifukwa mumafanana ndi manda opaka laimu,+ amene kunja kwake amaonekadi okongola, koma mkati mwake muli mafupa a anthu akufa ndi zonyansa zamitundu yonse. 28 Mofanana ndi zimenezi, pamaso pa anthu, inunso mumaoneka ngati olungama koma mkati mwanu mwadzaza chinyengo ndi kusamvera malamulo.+
29 Tsoka kwa inu alembi ndi Afarisi, anthu achinyengo inu!+ Chifukwa mumamanga manda a aneneri ndi kukongoletsa manda* a anthu olungama,+ 30 ndipo mumanena kuti, ‘Tikanakhalako mʼmasiku a makolo athu, ifeyo sitikanakhudzidwa ndi mlandu wawo wokhetsa magazi a aneneri.’ 31 Choncho mukudzichitira nokha umboni kuti ndinu ana a anthu amene anapha aneneri.+ 32 Ndiyetu malizitsani ntchito imene makolo anu anayamba.
33 Njoka inu, ana a mphiri,+ mudzathawa bwanji chiweruzo cha Gehena?*+ 34 Pa chifukwa chimenechi, ndikukutumizirani aneneri,+ anthu anzeru ndi aphunzitsi.+ Ena a iwo mudzawapha+ nʼkuwapachika pamtengo ndipo ena mudzawakwapula+ mʼmasunagoge mwanu ndi kuwazunza+ mumzinda ndi mzinda, 35 kuti magazi onse a anthu olungama amene anakhetsedwa padziko lapansi abwere pa inu. Kuyambira magazi a Abele wolungama+ mpaka magazi a Zekariya mwana wa Barakiya, amene inu munamupha pakati pa nyumba yopatulika ndi guwa lansembe.+ 36 Ndithu ndikukuuzani kuti, mʼbadwo uwu udzayankha mlandu wa zinthu zonsezi.
37 Yerusalemu, Yerusalemu, wopha aneneri iwe ndi woponya miyala anthu otumizidwa kwa iwe.+ Mobwerezabwereza ndinafuna kusonkhanitsa ana ako pamodzi, ngati mmene nkhuku yathadzi imasonkhanitsira anapiye ake mʼmapiko. Koma anthu inu simunafune zimenezo.+ 38 Tsopano tamverani! Mulungu wachoka nʼkukusiyirani nyumba yanuyi.*+ 39 Ndithu ndikukuuzani, kuyambira panopa simudzandionanso mpaka pamene mudzanene kuti, ‘Wodalitsidwa ndi amene akubwera mʼdzina la Yehova!’”*+
24 Pamene Yesu ankachoka kukachisi, ophunzira ake anabwera kwa iye kuti amuonetse nyumba zapakachisipo. 2 Koma iye anawauza kuti: “Kodi simukuziona zinthu zonsezi? Ndithu ndikukuuzani, pano sipadzatsala mwala uliwonse pamwamba pa mwala unzake umene sudzagwetsedwa.”+
3 Atakhala pansi mʼphiri la Maolivi, ophunzira anabwera kwa iye ali payekha nʼkumufunsa kuti: “Tiuzeni, kodi zinthu zimenezi zidzachitika liti, ndipo chizindikiro cha kukhalapo* kwanu+ ndi cha mapeto a nthawi* ino+ chidzakhala chiyani?”
4 Poyankha Yesu ananena kuti: “Samalani kuti munthu asakusocheretseni,+ 5 chifukwa ambiri adzabwera mʼdzina langa nʼkunena kuti, ‘Khristu uja ndine,’ ndipo adzasocheretsa anthu ambiri.+ 6 Mudzamva phokoso la nkhondo ndi malipoti a nkhondo. Izitu zisadzakuchititseni mantha, chifukwa zimenezi zikuyenera kuchitika ndithu, koma mapeto adzakhala asanafikebe.+
7 Mtundu udzaukirana ndi mtundu wina ndipo ufumu udzaukirana ndi ufumu wina.+ Kudzakhala njala+ ndi zivomerezi mʼmalo osiyanasiyana.+ 8 Zonsezi ndi chiyambi cha mavuto aakulu.*
9 Kenako anthu adzakuperekani kuti mukazunzidwe+ ndipo adzakuphani.+ Anthu a mitundu yonse adzadana nanu chifukwa cha dzina langa.+ 10 Pa nthawiyo anthu ambiri adzapunthwa ndipo adzaperekana komanso kudana. 11 Kudzakhala aneneri ambiri abodza ndipo adzasocheretsa anthu ambiri.+ 12 Chifukwa cha kuwonjezeka kwa kusamvera malamulo, chikondi cha anthu ambiri chidzazirala. 13 Koma amene adzapirire* mpaka pamapeto ndi amene adzapulumuke.+ 14 Ndipo uthenga wabwino uwu wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni kwa anthu amitundu yonse,+ kenako mapeto adzafika.
15 Choncho mukadzaona chinthu chonyansa chobweretsa chiwonongeko, chimene mneneri Danieli ananena, chitaima mʼmalo oyera+ (wowerenga adzazindikire), 16 amene ali mu Yudeya adzayambe kuthawira kumapiri.+ 17 Munthu amene ali padenga la nyumba asadzatsike kukatenga katundu mʼnyumba mwake. 18 Munthu amene ali mʼmunda asadzabwerere kukatenga malaya ake akunja. 19 Tsoka kwa akazi oyembekezera komanso oyamwitsa ana mʼmasiku amenewo! 20 Pitirizani kupemphera kuti musadzathawe mʼnyengo ya chisanu kapena pa tsiku la Sabata. 21 Chifukwa pa nthawiyo kudzakhala chisautso chachikulu+ chimene sichinachitikepo kuchokera pachiyambi cha dziko mpaka lero, ndipo sichidzachitikanso.+ 22 Kunena zoona, masikuwo akanapanda kufupikitsidwa, palibe amene akanapulumuka. Koma chifukwa cha osankhidwawo, masikuwo adzafupikitsidwa.+
23 Choncho munthu akadzakuuzani kuti, ‘Onani! Khristu uja ali kuno,’+ kapena, ‘Ali uko!’ musadzakhulupirire zimenezo.+ 24 Chifukwa kudzabwera anthu onamizira kuti ndi Khristu komanso aneneri abodza+ ndipo adzachita zizindikiro zamphamvu ndiponso zodabwitsa, kuti ngati nʼkotheka, adzasocheretse+ ngakhale osankhidwawo. 25 Onani! Ine ndakuchenjezani zimenezi zisanachitike. 26 Choncho anthu akadzakuuzani kuti, ‘Taonani! Ali mʼchipululu,’ musadzapiteko. Akadzati, ‘Taonani! Ali mʼzipinda zamkati,’ musadzakhulupirire zimenezo.+ 27 Chifukwa mofanana ndi mmene mphezi imangʼanimira kuchokera kumʼmawa nʼkuwala mpaka kukafika kumadzulo, zidzakhalanso choncho ndi kukhalapo* kwa Mwana wa munthu.+ 28 Kulikonse kumene kuli chinthu chakufa, ziwombankhanga zidzasonkhana komweko.+
29 Chisautso cha masiku amenewo chikadzangotha, dzuwa lidzachita mdima+ ndipo mwezi sudzapereka kuwala kwake. Nyenyezi zidzagwa kuchokera kumwamba ndipo mphamvu zakumwamba zidzagwedezeka.+ 30 Kenako chizindikiro cha Mwana wa munthu chidzaonekera kumwamba ndipo mafuko onse apadziko lapansi adzadziguguda pachifuwa chifukwa cha chisoni.+ Iwo adzaona Mwana wa munthu+ akubwera pamitambo ya kumwamba ndi mphamvu ndiponso ulemerero waukulu.+ 31 Iye adzatumiza angelo ake ndi kulira kwamphamvu kwa lipenga ndipo adzasonkhanitsa osankhidwa ake kuchokera kumphepo 4, kuchokera kumalekezero amumlengalenga mpaka kumalekezero ena.+
32 Tsopano phunzirani zokhudza mtengo wa mkuyu kuchokera pa fanizo ili: Nthambi yake yanthete ikaphuka nʼkuchita masamba, mumadziwa kuti chilimwe chili pafupi.+ 33 Chimodzimodzi inunso, mukadzaona zinthu zonsezi, mudzadziwe kuti iye ali pafupi, ali pakhomo penipeni.+ 34 Ndithu ndikukuuzani kuti mʼbadwo uwu sudzatha wonse kufa, mpaka zinthu zonsezi zitachitika. 35 Kumwamba ndi dziko lapansi zidzachoka, koma mawu anga adzakhalapo mpaka kalekale.+
36 Kunena za tsiku limenelo ndi ola lake, palibe amene akudziwa,+ ngakhale angelo akumwamba kapenanso Mwana, kupatulapo Atate wokha.+ 37 Chifukwa mofanana ndi mmene masiku a Nowa analili,+ ndi mmenenso kukhalapo* kwa Mwana wa munthu kudzakhalire.+ 38 Mʼmasiku amenewo Chigumula chisanafike, anthu ankadya ndi kumwa. Amuna ankakwatira ndipo akazi ankakwatiwa mpaka tsiku limene Nowa analowa mʼchingalawa.+ 39 Anthu ananyalanyaza zimene zinkachitika mpaka Chigumula chinafika nʼkuwaseseratu onsewo.+ Zidzakhalanso choncho ndi kukhalapo kwa Mwana wa munthu. 40 Pa nthawiyo, amuna awiri adzakhala ali mʼmunda. Mmodzi adzatengedwa ndipo winayo adzasiyidwa. 41 Akazi awiri adzakhala akupera pamphero. Mmodzi adzatengedwa ndipo winayo adzasiyidwa.+ 42 Choncho khalanibe maso chifukwa simukudziwa tsiku limene Ambuye wanu adzabwere.+
43 Koma dziwani izi: Ngati mwininyumba atadziwa nthawi imene wakuba angabwere,+ angakhale maso ndipo sangalole kuti wakubayo athyole nʼkulowa mʼnyumba mwake.+ 44 Pa chifukwa chimenechi, inunso khalani okonzeka,+ chifukwa Mwana wa munthu adzabwera pa ola limene simukuliganizira.
45 Kodi ndi ndani kwenikweni amene ndi kapolo wokhulupirika komanso wanzeru amene mbuye wake anamuika kuti aziyangʼanira antchito ake apakhomo, nʼkumawapatsa chakudya pa nthawi yoyenera?+ 46 Kapolo ameneyo adzakhala wosangalala, ngati mbuye wake pobwera adzamupeze akuchita zimenezo!+ 47 Ndithu ndikukuuzani, adzamuika kuti aziyangʼanira zinthu zake zonse.
48 Koma ngati kapolo ameneyu angasonyeze kuti ndi woipa nʼkuyamba kunena mumtima mwake kuti, ‘Mbuye wanga akuchedwa,’+ 49 nʼkuyamba kumenya akapolo anzake komanso kudya ndi kumwa limodzi ndi zidakwa zenizeni, 50 mbuye wa kapoloyo adzabwera pa tsiku limene iye sakuyembekezera ndi pa ola limene sakulidziwa.+ 51 Choncho adzamupatsa chilango choopsa ndipo adzamuponya kumene kuli anthu achinyengo. Kumeneko iye adzalira komanso kukukuta mano.”+
25 “Ufumu wakumwamba tingauyerekezere ndi anamwali 10 amene anatenga nyale zawo+ nʼkupita kukachingamira mkwati.+ 2 Anamwali 5 anali opusa ndipo 5 anali ochenjera.*+ 3 Opusawo anatenga nyale zawo koma sanatenge mafuta owonjezera. 4 Koma ochenjerawo anatenga mafuta owonjezera mʼmabotolo awo limodzi ndi nyale zawo. 5 Popeza mkwati anachedwa kubwera, onse anayamba kusinza kenako anagona. 6 Pakati pa usiku kunamveka mawu ofuula akuti: ‘Mkwati uja wafika! Tulukani mukamuchingamire.’ 7 Nthawi yomweyo anamwali onsewo anadzuka nʼkukonza nyale zawo.+ 8 Opusa aja anauza ochenjera kuti, ‘Tigawireniko mafuta anu, chifukwa nyale zathu zatsala pangʼono kuzima.’ 9 Ochenjerawo anayankha kuti: ‘Mwina satikwanira tikagawana ndi inu. Pitani kwa ogulitsa kuti mukagule anu.’ 10 Atanyamuka kupita kukagula mafutawo, mkwati anafika. Anamwali amene anali atakonzeka aja analowa naye limodzi mʼnyumba imene munali phwando laukwati+ ndipo chitseko chinatsekedwa. 11 Pambuyo pake anamwali ena aja nawonso anafika nʼkunena kuti, ‘Ambuye, ambuye, titsegulireni!’+ 12 Iye anawayankha kuti, ‘Kunena zoona, sindikukudziwani.’
13 Choncho pitirizani kukhala maso+ chifukwa simukudziwa tsiku kapena ola lake.+
14 Chifukwa zili ngati munthu amene ankafuna kupita kudziko lina, ndipo anaitanitsa akapolo ake nʼkuwasungitsa chuma chake.+ 15 Woyamba anamupatsa ndalama zokwana matalente* 5, wachiwiri anamupatsa matalente awiri ndipo wachitatu anamupatsa talente imodzi. Aliyense anamupatsa mogwirizana ndi luso lake ndipo iye anapita kudziko lina. 16 Nthawi yomweyo amene analandira matalente 5 uja ananyamuka kukachita nawo malonda ndipo anapindula matalente enanso 5. 17 Chimodzimodzinso amene analandira matalente awiri uja, anapindula enanso awiri. 18 Koma kapolo amene analandira imodzi yokha uja anapita kukakumba pansi nʼkubisa ndalama* ya mbuye wakeyo.
19 Patapita nthawi yaitali, mbuye wa akapolowo anabwera nʼkuwerengerana nawo ndalama.+ 20 Choncho amene analandira matalente 5 uja anabwera ndi matalente ena owonjezera 5 nʼkunena kuti, ‘Ambuye, paja munandipatsa matalente 5 koma onani, ndapindula matalente enanso 5.’+ 21 Mbuye wakeyo anamuyankha kuti: ‘Wachita bwino kwambiri, ndiwe kapolo wabwino komanso wokhulupirika! Unakhulupirika pa zinthu zochepa, ndikuika kuti uziyangʼanira zinthu zambiri.+ Sangalala limodzi ndi ine mbuye wako.’+ 22 Kenako kunabwera kapolo amene analandira matalente awiri uja nʼkunena kuti, ‘Ambuye, paja munandipatsa matalente awiri koma taonani, ndapindula matalente enanso awiri.’+ 23 Mbuye wake anamuyankha kuti: ‘Wachita bwino kwambiri, ndiwe kapolo wabwino komanso wokhulupirika! Unakhulupirika pa zinthu zochepa, ndikuika kuti uziyangʼanira zinthu zambiri. Sangalala limodzi ndi ine mbuye wako.’
24 Pa mapeto pake kunabwera kapolo amene analandira talente imodzi uja, ndipo anati: ‘Ambuye, ndinkadziwa kuti inu ndinu munthu wovuta. Mumakolola kumene simunafese ndipo mumatuta tirigu kumene simunapete.+ 25 Choncho ndinachita mantha ndipo ndinapita kukabisa talente yanu ija pansi. Ndalama yanu iyi, landirani.’ 26 Mbuye wakeyo anayankha kuti: ‘Kapolo woipa ndi waulesi iwe! Ukuti unkadziwa kuti ineyo ndimakolola kumene sindinafese ndi kututa tirigu kumene sindinapete? 27 Ndiyetu zikanakhala bwino ukanasungitsa ndalama* zangazo kwa osunga ndalama, ndipo ine pobwera ndikanalandira ndalamazo limodzi ndi chiwongoladzanja chake.
28 Choncho mulandeni talenteyo nʼkuipereka kwa amene ali ndi matalente 10.+ 29 Chifukwa aliyense amene ali nazo, adzapatsidwa zinanso zambiri ndipo adzakhala ndi zochuluka. Koma amene alibe adzalandidwa ngakhalenso zimene ali nazo.+ 30 Ponyani kapolo wopanda pake ameneyu kunja kumdima. Kumeneko akalira ndi kukukuta mano.’
31 Mwana wa munthu+ akadzabwera mu ulemerero wake, limodzi ndi angelo onse,+ adzakhala pampando wake wachifumu waulemerero. 32 Mitundu yonse ya anthu idzasonkhanitsidwa kwa iye ndipo adzalekanitsa anthu, mofanana ndi mmene mʼbusa amalekanitsira nkhosa ndi mbuzi. 33 Adzaika nkhosa+ kudzanja lake lamanja koma mbuzi adzaziika kudzanja lake lamanzere.+
34 Kenako Mfumu idzauza amene ali kudzanja lake lamanja kuti: ‘Bwerani, inu amene mwadalitsidwa ndi Atate wanga. Lowani mu Ufumu umene anakukonzerani kuchokera pachiyambi cha dziko lapansi.* 35 Chifukwa ndinamva njala koma inu munandipatsa chakudya. Ndinamva ludzu koma inu munandipatsa chakumwa. Ndinali mlendo koma inu munandilandira bwino.+ 36 Ndinali wamaliseche* koma inu munandiveka.+ Ndinadwala koma inu munandisamalira. Ndinali mʼndende koma inu munabwera kudzandiona.’+ 37 Ndiyeno olungamawo adzamuyankha kuti: ‘Ambuye, tinakuonani liti muli wanjala ife nʼkukudyetsani, kapena muli waludzu, ife nʼkukupatsani chakumwa?+ 38 Tinakuonani liti muli mlendo ife nʼkukulandirani bwino, kapena muli wamaliseche ife nʼkukuvekani? 39 Tinakuonani liti mukudwala kapena tinabwera liti kudzakuonani muli mʼndende?’ 40 Koma poyankha Mfumuyo idzawauza kuti, ‘Ndithu ndikukuuzani, nthawi iliyonse imene munachitira zimenezo mmodzi wa abale anga aangʼono awa, munachitiranso ine.’+
41 Kenako adzauza amene ali kumanzere kwake kuti, ‘Chokani pamaso panga+ anthu otembereredwa inu. Pitani kumoto wosatha+ umene anakolezera Mdyerekezi ndi angelo ake.+ 42 Chifukwa ndinamva njala koma inu simunandipatse chakudya. Ndinamva ludzu koma inu simunandipatse chakumwa. 43 Ndinali mlendo koma inu simunandilandire bwino. Ndinali wamaliseche koma inu simunandiveke. Ndinadwala komanso ndinali mʼndende koma inu simunandisamalire.’ 44 Iwonso adzayankha kuti: ‘Ambuye, tinakuonani liti muli ndi njala kapena muli ndi ludzu kapena muli mlendo kapena muli wamaliseche kapena mukudwala kapena muli mʼndende ife osakutumikirani?’ 45 Kenako iye adzawayankha kuti: ‘Ndithu ndikukuuzani, nthawi iliyonse imene simunachitire zimenezo mmodzi wa aangʼono awa, simunachitirenso ine.’+ 46 Anthu amenewa adzachoka kupita kuchiwonongeko chosatha,*+ koma olungama kumoyo wosatha.”+
26 Yesu atamaliza kunena zinthu zonsezi, anauza ophunzira ake kuti: 2 “Inu mukudziwa kuti Pasika achitika pakangopita masiku awiri+ ndipo Mwana wa munthu aperekedwa kuti akapachikidwe.”+
3 Pa nthawiyi, ansembe aakulu ndiponso akulu anasonkhana mʼbwalo lapanyumba ya mkulu wa ansembe dzina lake Kayafa.+ 4 Iwo anapangana+ zoti agwire* Yesu mochenjera nʼkumupha. 5 Koma ankanena kuti: “Tisadzamugwire pachikondwerero kuopera kuti anthu angadzachite chipolowe.”
6 Pa nthawi imene Yesu anali ku Betaniya mʼnyumba mwa Simoni wakhate,+ 7 kunafika mayi wina atatenga botolo lopangidwa ndi mwala wa alabasitala muli mafuta onunkhira okwera mtengo ndipo anayamba kuthira mafutawo mʼmutu mwa Yesu pamene iye ankadya patebulo. 8 Ophunzira ake ataona zimenezi anakwiya nʼkunena kuti: “Akuwonongeranji mafutawa? 9 Mafuta amenewa akanagulitsidwa ndalama zambiri ndipo ndalamazo zikanaperekedwa kwa anthu osauka.” 10 Yesu anadziwa zimenezi ndipo anawauza kuti: “Nʼchifukwa chiyani mukumuvutitsa mayiyu? Iyetu wandichitira zinthu zabwino. 11 Osaukawo muli nawo nthawi zonse,+ koma ine simudzakhala nane nthawi zonse.+ 12 Zimene mayiyu wachita pothira mafuta onunkhirawa pathupi langa, wazichita pokonzekera kuikidwa mʼmanda kwanga.+ 13 Ndithu ndikukuuzani, kulikonse kumene uthenga wabwino udzalalikidwe padziko lonse, anthu azidzanena zimene mayiyu wachita kuti azidzamukumbukira.”+
14 Kenako mmodzi wa ophunzira 12 aja, amene ankadziwika kuti Yudasi Isikariyoti,+ anapita kwa ansembe aakulu+ 15 nʼkuwafunsa kuti: “Kodi mudzandipatsa chiyani ndikamupereka kwa inu?”+ Iwo anamulonjeza ndalama 30 zasiliva.+ 16 Choncho kuyambira nthawi imeneyo anayesetsa kufunafuna mpata wabwino kuti amupereke.
17 Pa tsiku loyamba la chikondwerero cha Mikate Yopanda Zofufumitsa,+ ophunzira anabwera kwa Yesu nʼkumufunsa kuti: “Kodi mukufuna tikakukonzereni kuti malo odyerako Pasika?”+ 18 Iye anati: “Pitani mumzinda kwa Munthu wakutiwakuti ndipo mukamuuze kuti, ‘Mphunzitsi wanena kuti: “Nthawi yanga yoikidwiratu yayandikira. Ndidzachita phwando la Pasika pamodzi ndi ophunzira anga kunyumba kwako.”’” 19 Choncho ophunzirawo anachitadi mogwirizana ndi zimene Yesu anawauza ndipo anakonza zinthu zonse zofunika pa Pasika.
20 Nthawi yamadzulo,+ iye ndi ophunzira ake 12 aja anakhala patebulo nʼkumadya chakudya.+ 21 Akudya chakudyacho iye ananena kuti: “Ndithu ndikukuuzani, mmodzi wa inu andipereka.”+ 22 Chifukwa chomva chisoni kwambiri ndi zimenezi, aliyense anayamba kumufunsa kuti: “Ambuye, kodi ndine kapena?” 23 Iye anayankha kuti: “Amene akusunsa nane limodzi mʼmbalemu ndi amene andipereke.+ 24 Zoonadi, Mwana wa munthu achoka, mogwirizana ndi zimene Malemba amanena za iye. Koma tsoka+ kwa munthu amene akupereka Mwana wa munthu!+ Zikanakhala bwino kwa munthu ameneyu ngati akanapanda kubadwa.”+ 25 Yudasi amene anali atatsala pangʼono kumupereka anayankha kuti: “Nanga nʼkukhala ine Rabi?” Yesu anamuyankha kuti: “Wanena wekha.”
26 Akupitiriza kudya, Yesu anatenga mkate ndipo atayamika Mulungu, anaunyemanyema+ nʼkuupereka kwa ophunzira ake. Iye ananena kuti: “Eni, idyani. Mkate uwu ukuimira thupi langa.”+ 27 Kenako anatenga kapu ya vinyo ndipo atayamika, anaipereka kwa iwo nʼkunena kuti: “Imwani nonsenu.+ 28 Vinyoyu akuimira ‘magazi anga+ a pangano,’+ amene adzakhetsedwe chifukwa cha anthu ambiri+ kuti machimo awo akhululukidwe.+ 29 Koma ndikukuuzani kuti: Sindidzamwanso chakumwa chilichonse chochokera ku mphesa ngati ichi mpaka tsiku limene ndidzamwe chatsopano limodzi ndi inu mu Ufumu wa Atate wanga.”+ 30 Pamapeto pake, atamaliza kuimba nyimbo zotamanda Mulungu,* anatuluka nʼkupita kuphiri la Maolivi.+
31 Kenako Yesu anawauza kuti: “Nonsenu muthawa nʼkundisiya ndekha usiku uno, chifukwa Malemba amanena kuti: ‘Ndidzapha mʼbusa ndipo nkhosa zamʼgululo zidzabalalika.’+ 32 Koma ndikadzauka kwa akufa, ndidzatsogola kukafika ku Galileya inu musanafikeko.”+ 33 Koma Petulo anamuyankha kuti: “Ngakhale ena onse atathawa nʼkukusiyani, ine ndekha sindingathawe!”+ 34 Yesu anamuuza kuti: “Ndithudi ndikukuuza iwe, usiku womwe uno tambala asanalire, undikana katatu.”+ 35 Petulo anayankha kuti: “Ngati kuli kufa, ine ndifa nanu limodzi, sindingakukaneni.”+ Ophunzira ena onse ananenanso chimodzimodzi.
36 Kenako Yesu anafika nawo pamalo otchedwa Getsemane,+ ndipo anauza ophunzirawo kuti: “Khalani pansi panopa, ine ndikupita uko kukapemphera.”+ 37 Popita kumeneko anatenga Petulo ndi ana awiri a Zebedayo. Ndipo anayamba kumva chisoni komanso kuvutika kwambiri mumtima mwake.+ 38 Kenako anawauza kuti: “Ine ndikumva chisoni* chofa nacho. Khalani pompano ndipo mukhalebe maso pamodzi ndi ine.”+ 39 Choncho atapita patsogolo pangʼono, anagwada mpaka nkhope yake pansi ndipo anapemphera kuti:+ “Atate wanga, ngati nʼkotheka lolani kuti kapu iyi+ indipitirire. Koma osati mwa kufuna kwanga, koma mwa kufuna kwanu.”+
40 Atatero anabwerera pamene panali ophunzira ake aja ndipo anawapeza akugona. Choncho anafunsa Petulo kuti: “Zoona simungathe kukhalabe maso limodzi ndi ine kwa ola limodzi?+ 41 Khalani maso+ ndipo mupitirize kupemphera+ kuti musalowe mʼmayesero.+ Zoona, mzimu ndi wofunitsitsa, koma thupi ndi lofooka.”+ 42 Anachokanso kachiwiri nʼkupita kukapemphera kuti: “Atate wanga, ngati sizingatheke kuti kapuyi indipitirire mpaka nditamwa ndithu, zimene inu mukufuna zichitike.”+ 43 Anabweranso nʼkuwapeza akugona, chifukwa zikope zawo zinali zitalemera. 44 Choncho anawasiya nʼkupitanso kukapemphera kachitatu ndipo anabwereza mawu omwe aja. 45 Kenako anabwerera kwa ophunzira aja nʼkuwauza kuti: “Zoona nthawi ngati ino mukugona ndi kupumula? Taonani! Nthawi yoti Mwana wa munthu aperekedwe mʼmanja mwa anthu ochimwa yayandikira. 46 Nyamukani, tiyeni tizipita. Onani! Wondipereka uja ali pafupi.” 47 Mawu adakali mʼkamwa, Yudasi, mmodzi wa ophunzira 12 aja, anafika limodzi ndi gulu lalikulu la anthu kuchokera kwa ansembe aakulu ndi kwa akulu, atanyamula malupanga ndi zibonga.+
48 Apa nʼkuti womuperekayu atawapatsa chizindikiro chakuti: “Amene ndikamukise ndi yemweyo, mukamugwire.” 49 Atafika, Yudasi analunjika kwa Yesu nʼkunena kuti: “Moni Rabi!” Ndipo anamukisa. 50 Koma Yesu anamufunsa kuti: “Bwanawe, wabwera kudzatani kuno?”+ Nthawi yomweyo iwo anayandikira ndipo anagwira Yesu nʼkumumanga. 51 Koma mmodzi mwa anthu amene anali ndi Yesu anasolola lupanga lake nʼkutema nalo kapolo wa mkulu wa ansembe mpaka kuduliratu khutu lake.+ 52 Ndiyeno Yesu anamuuza kuti: “Bwezera lupanga lako mʼchimake,+ chifukwa onse ogwira lupanga adzafa ndi lupanga.+ 53 Kapena ukuganiza kuti sindingapemphe Atate wanga kuti anditumizire magulu ankhondo oposa 12 a angelo nthawi yomwe ino?+ 54 Koma ndikachita zimenezo, nanga Malemba amene amanena kuti zimenezi ziyenera kuchitika adzakwaniritsidwa bwanji?” 55 Mu ola lomwelo Yesu anafunsa gulu la anthulo kuti: “Bwanji mwabwera kudzandigwira mutatenga malupanga ndi zibonga ngati mukudzalimbana ndi wachifwamba? Tsiku ndi tsiku ndinkakhala pansi mʼkachisi nʼkumaphunzitsa,+ koma simunandigwire.+ 56 Koma zonsezi zachitika kuti zimene aneneri analemba zikwaniritsidwe.”*+ Kenako ophunzira ake onse anamuthawa nʼkumusiya yekha.+
57 Anthu amene anagwira Yesu aja anapita naye kwa Kayafa+ mkulu wa ansembe, kumene alembi ndi akulu anali atasonkhana.+ 58 Koma Petulo anapitiriza kumutsatira ali chapatali ndithu, mpaka anafika mʼbwalo lapanyumba ya mkulu wa ansembeyo. Atalowa mkati, anakhala pansi limodzi ndi antchito amʼnyumbamo kuti aone zotsatira zake.+
59 Ndiyeno ansembe aakulu ndi Khoti lonse Lalikulu la Ayuda* ankafunafuna umboni wabodza kuti anamizire Yesu mlandu nʼcholinga choti amuphe.+ 60 Koma sanaupeze ngakhale kuti kunabwera mboni zambiri zabodza.+ Patapita nthawi, kunabwera mboni zina ziwiri 61 nʼkunena kuti: “Munthu ameneyu ananena kuti, ‘Ndikhoza kugwetsa kachisi wa Mulungu nʼkumumanganso mʼmasiku atatu.’”+ 62 Atamva zimenezo mkulu wa ansembe anaimirira nʼkumufunsa kuti: “Kodi suyankha? Kodi sukumva zimene anthuwa akukunenezazi?”+ 63 Koma Yesu anangokhala chete.+ Choncho mkulu wa ansembe anamuuza kuti: “Ndikukulumbiritsa pali Mulungu wamoyo, utiuze ngati ndiwedi Khristu, Mwana wa Mulungu!”+ 64 Yesu anamuyankha kuti: “Mwanena nokha. Koma ndikukuuzani kuti: Kuyambira panopa mpaka mʼtsogolo mudzaona Mwana wa munthu+ atakhala kudzanja lamanja lamphamvu.+ Mudzamuonanso akubwera pamitambo yakumwamba.”+ 65 Kenako mkulu wa ansembe anangʼamba malaya ake akunja nʼkunena kuti: “Wanyoza Mulungu! Nanga tingafunenso mboni zina pamenepa? Pano mwadzimvera nokha mmene akunyozera Mulungu. 66 Ndiye inu mukuona bwanji pamenepa?” Iwo anayankha kuti: “Akuyenera kufa basi.”+ 67 Ndiyeno anayamba kumulavulira kunkhope+ komanso kumumenya nkhonya.+ Ena anamuwomba mbama+ 68 nʼkunena kuti: “Losera tione Khristu iwe. Wakumenya ndi ndani?”
69 Tsopano Petulo anali atakhala pansi mʼbwalolo ndipo mtsikana wina wantchito anabwera kwa iye nʼkunena kuti: “Inunso munali ndi Yesu wa ku Galileyayu!”+ 70 Koma iye anakana pamaso pa onse kuti: “Sindikudziwa zimene ukunena.” 71 Atatuluka nʼkupita pakanyumba kapageti, mtsikana winanso anamuzindikira nʼkuuza ena amene anali pafupi kuti: “Bambo awa anali limodzi ndi Yesu Mnazaretiyu.”+ 72 Apanso Petulo anakana mochita kulumbira ndipo ananena kuti: “Ndithudi munthu ameneyu ine sindikumudziwa ayi!” 73 Patapita kanthawi pangʼono, amene anali ataimirira chapafupi anabwera nʼkuuza Petulo kuti: “Ndithu iwenso uli mʼgulu la ophunzira ake ndipo kalankhulidwe kako kakugwiritsa.” 74 Pamenepo iye anayamba kutemberera ndi kulumbira kuti: “Munthu ameneyu ine sindikumudziwa ayi!” Nthawi yomweyo tambala analira. 75 Ndiyeno Petulo anakumbukira mawu a Yesu aja akuti: “Tambala asanalire, udzandikana katatu.”+ Ndipo anatuluka panja nʼkuyamba kulira mopwetekedwa mtima kwambiri.
27 Mʼmawa kutacha, ansembe aakulu onse limodzi ndi akulu a anthu anakambirana nʼkugwirizana kuti aphe Yesu.+ 2 Ndipo atamumanga, anapita kukamupereka kwa Bwanamkubwa Pilato.+
3 Kenako Yudasi amene anamupereka uja, ataona kuti Yesu waweruzidwa kuti aphedwe, anavutika koopsa mumtima moti anapita kukabweza ndalama 30 zasiliva zija kwa ansembe aakulu ndiponso akulu.+ 4 Iye anati: “Ndachimwa popereka munthu wosalakwa.”* Iwo anamuyankha kuti: “Ife sizikutikhudza zimenezo. Udziwa wekha chochita!”* 5 Choncho iye anaponya ndalama zasiliva zija mʼkachisi nʼkuchoka. Kenako anapita kukadzimangirira.+ 6 Koma ansembe aakulu anatenga ndalama zasilivazo nʼkunena kuti: “Nʼzosaloleka kuti ndalamazi ziikidwe mʼmalo opatulika osungiramo chuma, chifukwa ndi malipiro a magazi.” 7 Atakambirana, anagwiritsa ntchito ndalamazo pogulira munda wa woumba mbiya kuti ukhale manda a alendo. 8 Choncho munda umenewu umatchedwa Munda wa Magazi+ mpaka lero. 9 Zimenezi zinakwaniritsa mawu amene Mulungu ananena kudzera mwa mneneri Yeremiya* kuti: “Ndipo anatenga ndalama 30 zasiliva, mtengo wogulira munthu, mtengo umene ena mwa ana a Isiraeli anamuikira, 10 ndipo anagulira munda wa woumba mbiya, mogwirizana ndi zimene Yehova* anandilamula.”+
11 Tsopano Yesu anaimirira pamaso pa bwanamkubwa ndipo bwanamkubwayo anamufunsa kuti: “Kodi ndiwe Mfumu ya Ayuda?” Yesu anayankha kuti: “Zili choncho, monga mmene mwanenera.”+ 12 Koma pamene ansembe aakulu komanso akulu ankamuneneza, iye sanayankhe chilichonse.+ 13 Ndiyeno Pilato anamufunsa kuti: “Kodi sukumva zinthu zambirimbiri zimene akukunenezazi?” 14 Koma iye anangokhala chete, osamuyankha chilichonse, moti bwanamkubwayo anadabwa kwambiri.
15 Pa chikondwerero chilichonse, bwanamkubwayu ankamasulira anthu mkaidi mmodzi amene anthuwo akufuna.+ 16 Ndiye pa nthawiyi panali mkaidi wina woopsa kwambiri, dzina lake Baraba. 17 Choncho anthu atasonkhana pamodzi, Pilato ananena kuti: “Kodi mukufuna kuti ndikumasulireni ndani, Baraba kapena Yesu amene mumati ndi Khristu?” 18 Chifukwa Pilato ankadziwa kuti anamupereka chifukwa cha kaduka. 19 Komanso atakhala pampando woweruzira milandu, mkazi wake anamutumizira uthenga wakuti: “Nkhani ya munthu wolungamayu isakukhudzeni chifukwa ine ndavutika kwambiri lero ndi maloto okhudza iyeyu.” 20 Komabe ansembe aakulu limodzi ndi akulu analimbikitsa anthu kupempha kuti awamasulire Baraba,+ koma kuti Yesu aphedwe.+ 21 Ndiyeno bwanamkubwayo anawafunsa kuti: “Kodi pa anthu awiriwa mukufuna kuti ndikumasulireni uti?” Iwo anati: “Baraba.” 22 Pilato anafunsanso kuti: “Nanga Yesu, amene mumati ndi Khristu uja, ndichite naye chiyani?” Onse anayankha kuti: “Apachikidwe ameneyo!”*+ 23 Iye anati: “Chifukwa chiyani? Kodi iyeyu walakwa chiyani?” Koma anthuwo anapitiriza kufuula mwamphamvu kuti: “Ameneyo apachikidwe basi!”+
24 Ataona kuti sizikuthandiza komanso kuti pakuyambika chipolowe, Pilato anangotenga madzi nʼkusamba mʼmanja pamaso pa gulu la anthulo ndipo ananena kuti: “Ine ndilibe mlandu wa magazi a munthu uyu. Zonse zili kwa inu.” 25 Atanena zimenezi anthu onse anayankha kuti: “Magazi ake akhale pa ife ndi pa ana athu.”+ 26 Choncho anawamasulira Baraba, koma analamula kuti Yesu akwapulidwe+ kenako anamupereka kuti akamuphe pomupachika pamtengo.+
27 Ndiyeno asilikali a bwanamkubwa anatenga Yesu nʼkulowa naye mʼnyumba ya bwanamkubwayo ndipo anasonkhanitsa gulu lonse la asilikali kwa iye.+ 28 Kumeneko anamuvula zovala zake nʼkumuveka chinsalu chofiira kwambiri.+ 29 Komanso analuka chisoti chachifumu chaminga nʼkumuveka kumutu ndipo anamupatsa bango mʼdzanja lake lamanja. Kenako anamugwadira nʼkumamunyoza kuti: “Moni, inu Mfumu ya Ayuda!” 30 Atatero anamulavulira+ ndipo anatenga bango lija nʼkuyamba kumumenya nalo mʼmutu. 31 Atamaliza kumunyozako, anamuvula chinsalu chija nʼkumuveka malaya ake akunja ndipo anapita naye kuti akamukhomerere pamtengo.+
32 Ali mʼnjira, anakumana ndi munthu wina wa ku Kurene, dzina lake Simoni. Iwo anakakamiza munthu ameneyu kuti asenze mtengo wozunzikirapo* wa Yesu.+ 33 Atafika pamalo otchedwa Gologota, kutanthauza kuti, Malo a Chibade,+ 34 anapatsa Yesu vinyo wosakaniza ndi zinthu zowawa zamadzimadzi kuti amwe,+ koma iye atalawa, anakana kumwa. 35 Atamukhomerera pamtengo, anagawana malaya ake akunja pochita maere+ 36 ndipo anakhala pansi nʼkumamuyangʼanira. 37 Komanso pamwamba pa mutu wake anakhomapo chikwangwani chosonyeza mlandu umene anamuphera kuti: “Uyu ndi Yesu, Mfumu ya Ayuda.”+
38 Ndiyeno achifwamba awiri anapachikidwa naye limodzi. Mmodzi anamupachika kudzanja lake lamanja ndipo wina anali kumanzere kwake.+ 39 Anthu amene ankadutsa pafupi ankanena mawu onyoza Yesu+ ndipo ankapukusa+ mitu yawo 40 nʼkumanena kuti: “Iwe amene unkanena kuti ungathe kugwetsa kachisi nʼkumumanga mʼmasiku atatu,+ dzipulumutse! Ngati ulidi mwana wa Mulungu, tsikatu pamtengo wozunzikirapowo!”*+ 41 Chimodzimodzinso ansembe aakulu limodzi ndi alembi komanso akulu. Nawonso anayamba kumunyoza nʼkumanena kuti:+ 42 “Ena anatha kuwapulumutsa, koma kuti adzipulumutse yekha zikumukanika! Ngati ali Mfumu ya Isiraeli,+ tiyeni tione ngati angatsike pamtengo wozunzikirapowo* ndipo ife timukhulupirira. 43 Paja iye amakhulupirira Mulungu, ndiye panopa Mulunguyo amupulumutse ngati akumufunadi+ chifukwa iye ankanena kuti, ‘Ine ndine Mwana wa Mulungu.’”+ 44 Nawonso achifwamba amene anapachikidwa naye limodzi ankamunyoza.+
45 Kuyambira cha mʼma 12 koloko masana* kunagwa mdima mʼdziko lonselo, mpaka 3 koloko masana.*+ 46 Cha mʼma 3 kolokomo, Yesu anafuula mwamphamvu kuti: “Eʹli, Eʹli, laʹma sa·bach·thaʹni?” kutanthauza kuti, “Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji ine?”+ 47 Ena mwa anthu amene anaimirira chapomwepo atamva zimenezi anayamba kunena kuti: “Munthuyu akuitana Eliya.”+ 48 Nthawi yomweyo mmodzi wa iwo anathamanga kukatenga siponji nʼkuiviika muvinyo wowawasa ndipo anaiika kubango nʼkumupatsa kuti amwe.+ 49 Koma enawo anati: “Mulekeni! Tione ngati Eliya angabwere kudzamupulumutsa.” 50 Ndiyeno Yesu anafuulanso mokweza mawu, kenako anatsirizika.+
51 Nthawi yomweyo nsalu yotchinga yamʼnyumba yopatulika+ inangʼambika pakati+ kuchokera pamwamba mpaka pansi.+ Dziko lapansi linagwedezeka ndipo matanthwe anangʼambika. 52 Manda* anatseguka ndipo mitembo yambiri ya anthu oyera amene anaikidwa mmenemo inaponyedwa kunja, 53 ndipo anthu ambiri anatha kuiona. (Pambuyo pa kuukitsidwa kwa Yesu, anthu amene ankachokera kumandako, analowa mumzinda woyera.) 54 Koma mtsogoleri wa asilikali ndi ena amene anali naye polondera Yesu ataona chivomerezicho ndi zimene zinkachitikazo, anachita mantha kwambiri ndipo anati: “Ndithu, uyu analidi Mwana wa Mulungu.”+
55 Komanso azimayi ambiri ochokera ku Galileya amene ankatsatira Yesu kuti azimutumikira, anali komweko nʼkumaonerera chapatali.+ 56 Ena mwa iwo anali Mariya wa ku Magadala, Mariya mayi a Yakobo ndi Yose, ndiponso panali mayi a Yakobo ndi Yohane.*+
57 Tsopano madzulo kwambiri, kunabwera munthu wina wachuma wa ku Arimateya, dzina lake Yosefe, amenenso anakhala wophunzira wa Yesu.+ 58 Iye anapita kwa Pilato kukapempha mtembo wa Yesu+ ndipo Pilato analamula kuti amupatse mtembowo.+ 59 Yosefe anatenga mtembowo nʼkuukulunga munsalu yoyera yabwino kwambiri,+ 60 ndipo anakauika mʼmanda*+ ake atsopano amene anawasema muthanthwe. Kenako atagubuduza chimwala chachikulu nʼkutseka pakhomo la mandawo,* anachoka. 61 Koma Mariya wa ku Magadala ndi Mariya wina anatsalira komweko, atakhala pansi pafupi ndi mandawo.+
62 Tsiku lotsatira, pambuyo pa Tsiku Lokonzekera,*+ ansembe aakulu ndi Afarisi anasonkhana pamaso pa Pilato, 63 nʼkunena kuti: “Bwana, ife takumbukira kuti munthu wachinyengo uja adakali moyo ananena kuti, ‘Pakadzadutsa masiku atatu ndidzaukitsidwa.’+ 64 Choncho lamulani kuti akhwimitse chitetezo pamandapo mpaka tsiku lachitatu, kuti ophunzira ake asabwere kudzamuba+ nʼkumauza anthu kuti, ‘Anaukitsidwa kwa akufa!’ Chifukwa chinyengo chotsirizachi chidzakhala choipa kwambiri kuposa choyamba chija.” 65 Pilato anawayankha kuti: “Tengani asilikali olondera awa. Pitani mukakhwimitse chitetezo monga mmene mukudziwira.” 66 Choncho anapita kukakhwimitsa chitetezo pamandawo potseka kwambiri mandawo ndi chimwala nʼkuikapo asilikali olondera.
28 Tsiku la Sabata litatha, mʼbandakucha wa tsiku loyamba la mlunguwo, Mariya wa ku Magadala ndi Mariya wina uja anabwera kudzaona manda.+
2 Atafika pafupi, anazindikira kuti pachitika chivomerezi champhamvu, chifukwa mngelo wa Yehova* anatsika kumwamba ndipo anafika nʼkugubuduza chimwala chija, nʼkukhala pachimwalapo.+ 3 Mngeloyo ankaoneka ngati mphezi ndipo zovala zake zinali zoyera kwambiri.+ 4 Alonda aja anachita mantha ndi mngeloyo ndipo ananjenjemera nʼkuuma gwa ngati afa.
5 Koma mngeloyo anauza azimayiwo kuti: “Inu musachite mantha, chifukwa ndikudziwa kuti mukufuna Yesu amene anaphedwa popachikidwa pamtengo.+ 6 Muno mulibe chifukwa waukitsidwa mogwirizana ndi zimene ananena.+ Bwerani muone pamene anagona. 7 Ndipo pitani mwamsanga mukauze ophunzira ake kuti waukitsidwa kwa akufa, moti panopa watsogola kupita ku Galileya.+ Kumeneko mukamuona. Umenewutu ndi uthenga wanga kwa inu.”+
8 Choncho iwo anachoka mwamsanga pamandapo ali ndi mantha ndiponso chimwemwe chochuluka ndipo anathamanga kukauza ophunzira ake.+ 9 Mwadzidzidzi Yesu anakumana nawo nʼkunena kuti: “Moni azimayi!” Kenako iwo anafika pafupi nʼkugwira mapazi ake ndipo anamuweramira mpaka nkhope zawo pansi. 10 Kenako Yesu anawauza kuti: “Musaope! Pitani mukauze abale anga kuti apite ku Galileya ndipo akandiona kumeneko.”
11 Iwo akupita, ena mwa alonda+ anapita mumzinda ndipo anakauza ansembe aakulu zonse zimene zinachitika. 12 Ansembe aakuluwo atakumana ndi akulu nʼkukambirana, anagwirizana zochita ndipo anapereka ndalama zasiliva zambiri kwa asilikaliwo 13 nʼkuwauza kuti: “Muzinena kuti, ‘Ophunzira ake anabwera usiku kudzamuba ife titagona.’+ 14 Ngati bwanamkubwa atamva zimenezi, timufotokozera nkhani yonse* ndipo inu simukuyenera kuda nkhawa.” 15 Choncho anatenga ndalama zasilivazo nʼkuchita mogwirizana ndi zimene anawauza ndipo nkhani imeneyi ndi yofala kwambiri pakati pa Ayuda mpaka lero.
16 Koma ophunzira 11 aja anapita ku Galileya,+ kuphiri kumene Yesu anawauza kuti akakumane nawo.+ 17 Atamuona anamugwadira, koma ena anakayikira ngati analidi iyeyo. 18 Tsopano Yesu anayandikira nʼkuwauza kuti: “Ulamuliro wonse waperekedwa kwa ine kumwamba ndi padziko lapansi.+ 19 Choncho pitani mukaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzira anga.+ Muziwabatiza+ mʼdzina la Atate, la Mwana ndi la mzimu woyera, 20 ndipo muziwaphunzitsa kuti azisunga zinthu zonse zimene ndinakulamulani.+ Ndipo dziwani kuti ine ndili limodzi ndi inu masiku onse mpaka mʼnyengo ya mapeto a nthawi* ino.”+
Kapena kuti, “Mesiya; Wodzozedwa.”
Kapena kuti, “mphamvu ya Mulungu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “anaganiza zothetsa ukwati mwachinsinsi.” Pa mwambo wachiyuda, kuti lonjezo loti anthu adzakwatirana lithe, ankatsatira dongosolo lothetsera ukwati.
Awa ndi malo oyamba mwa malo 237 mʼMalemba a Chigiriki pamene dzina la Mulungu lakuti Yehova likupezeka mʼBaibuloli. Onani Zakumapeto A5.
MʼChiheberi dzinali amati Yesuwa kapena kuti Yoswa ndipo limatanthauza kuti “Yehova Ndi Chipulumutso.”
Onani Zakumapeto A5.
Onani Zakumapeto A5.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Kapena kuti, “Mesiya; Wodzozedwa.”
Onani Zakumapeto A5.
Onani Zakumapeto A5.
Onani Zakumapeto A5.
Kapena kuti, “amene ankafuna moyo wa mwanayu.”
Nʼkutheka kuti dzinali likuchokera ku mawu a Chiheberi omwe angamasuliridwe kuti “Mphukira.”
Onani Zakumapeto A5.
Kapena kuti, “ankawaviika; ankawamiza.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “masandasi ake.”
“Mankhusu” ndi makoko amene amachotsa ku mbewu ngati mpunga popuntha ndipo amatha kuwauluza ndi mphepo.
Onani Zakumapeto A5.
Kapena kuti, “anamukweza pamalo okwera kwambiri a kachisi.”
Onani Zakumapeto A5.
Onani Zakumapeto A5.
MʼBaibulo, “nyanja ya Galileya” imatchulidwanso ndi mayina akuti, nyanja ya Kinereti, nyanja ya Genesarete komanso nyanja ya Tiberiyo.
Kapena kuti, “Chigawo cha Mizinda 10.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “chifukwa mphoto yanu ndi yaikulu kumwamba.”
Gehena ndi malo amene ankawotcherako zinyalala kunja kwa mzinda wa Yerusalemu. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mʼchilankhulo choyambirira, “kwadiranti yomalizira.” Onani Zakumapeto B14.
Mʼchilankhulo choyambirira, “limakupunthwitsa.”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
MʼChigiriki por·nei′a. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Onani Zakumapeto A5.
Onani Zakumapeto B14.
Kumeneku ndi kukongola popanda kupereka chiwongola dzanja.
Kapena kuti, “khalani okwanira.’ʼ
Kapena kuti, “mphatso kwa osauka.” Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Kapena kuti, “lizionedwa kuti ndi lopatulika; lizionedwa kuti ndi loyera.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mkate umene.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ngongole.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ali nafe ngongole.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Musatilowetse mʼmayesero.”
Kapena kuti, “amasiya kudzisamalira.”
Mawu a Chigiriki amene amasuliridwa kuti “njenjete” amatanthauza mtundu winawake wa kadziwotche amene amadya zovala.
Mʼchilankhulo choyambirira, “likulunjika.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “loipa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “amene angatalikitse moyo wake ndi mkono umodzi.” Onani Zakumapeto B14.
Mʼchilankhulo choyambirira, “atatentha thupi.”
Kapena kuti, “mʼmanda achikumbutso.”
Kapena kuti, “atakhala patebulo.”
Kapena kuti, “anakhala patebulo.”
“Petulo” amadziwika ndi mayina 5. Pano akutchulidwa kuti “Simoni, amene ankatchulidwa kuti Petulo.” Pa Mt 16:16 akutchulidwa kuti “Simoni Petulo,” pa Mac 15:14, “Sumiyoni,” ndipo pa Yoh 1:42, “Kefa.” Koma nthawi zambiri amatchulidwa kuti “Petulo,” monga mmene zilili pa Mt 14:28.
Kapena kuti, “wakhama.”
Kapena kuti, “mkuwa.”
Kapena kuti, “malaya owonjezera.”
Kapena kuti, “amene wapirira.”
Dzina limene Satana, yemwe ndi kalonga kapena kuti wolamulira ziwanda, amadziwika nalo.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mʼchilankhulo choyambirira, “asariyoni imodzi,” Onani Zakumapeto B14.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mʼchilankhulo choyambirira, “mwa onse amene anabadwa kwa akazi.”
Kapena kuti, “imaonekera kuti ndi yeniyeni.”
Kapena kuti, “chifukwa cha zotsatira zake.”
Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu ena.
Kapena kuti, “mkate wachionetsero.”
Dzina limene Satana, yemwe ndi kalonga kapena kuti wolamulira ziwanda amadziwika nalo.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Kapena kuti, “wosakhulupirika.”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
“Mpiru” umene watchulidwa pano umapezeka ku Palesitina. Kanjere kake kamakhala kakangʼono kwambiri koma kakamera, kamtengo kake kamatha kukula mpaka kufika mamita 4 ndipo kamakhala ndi nthambi.
Mabaibulo ena amati, “kuchokera pa chiyambi cha dziko lapansi.”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mʼchilankhulo choyambirira, “bwanamkubwa wa chigawo cha 4 cha dera.”
Ameneyu ndi Herode Antipa. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mʼchilankhulo choyambirira, “masitadiya ambiri.” Sitadiya imodzi inali yofanana ndi mamita 185.
Nthawi imeneyi inkayamba 3 koloko mpaka dzuwa litatuluka cha mʼma 6 koloko mʼmawa.
Izi sizikutanthauza kuti ankadya chakudya ndi mʼmanja mwakuda koma kuti sankatsatira miyambo ya Chiyuda yosambira mʼmanja.
MʼChigiriki por·nei′a. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Izi sizikutanthauza kuti ankadya chakudya ndi mʼmanja mwakuda koma kuti sankatsatira miyambo ya Chiyuda yosambira mʼmanja.
Kapena kuti, “azipita asanadye.”
Kapena kuti, “wosakhulupirika.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mnofu ndi magazi.”
Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu ena.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Kapena kuti, “adzakhalanso ndi moyo.”
Kapena kuti, “anayera.”
Onani Zakumapeto A3.
Onani Zakumapeto B14.
Mʼchilankhulo choyambirira, “khobidi la siteta.” Khobidi limeneli linali lofanana ndi madalakima 4. Onani Zakumapeto B14.
Kapena kuti, “kusintha.”
Kapena kuti, “limakupunthwitsa.”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Onani Zakumapeto A3.
Mabaibulo ena amati, “wanu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “upite ukamudzudzule.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ndi pakamwa pa mboni.”
Matalente 10,000 asiliva anali ofanana ndi madinari 60 miliyoni. Onani Zakumapeto B14.
Onani Zakumapeto B14.
Mʼchilankhulo choyambirira, “wachimanga mugoli limodzi.”
MʼChigiriki por·nei′a. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Kupha uku ndi kupha munthu mwachiwembu osati mwalamulo.
Kapena kuti, “kukhala wokwanira pamaso pa Mulungu.”
Onani Zakumapeto B14.
Mʼchilankhulo choyambirira, “ola lachitatu,” kuwerenga kuchokera mʼma 6 koloko mʼmawa.
Mʼchilankhulo choyambirira, “ola la 6 ndi ola la 9,” kuwerenga kuchokera mʼma 6 koloko mʼmawa.
Mʼchilankhulo choyambirira, “ola la 11,” kuwerenga kuchokera mʼma 6 koloko mʼmawa.
Onani Zakumapeto B14.
Onani Zakumapeto B14.
Onani Zakumapeto B14.
Mʼchilankhulo choyambirira, “ndi loipa.”
Kapena kuti, “wowolowa manja.”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mawu akuti “mwana wamkazi wa Ziyoni” ndi mawu andakatulo ndipo nthawi zambiri amanena za mzinda wa Yerusalemu kapena anthu amene ankakhala mumzindawo.
Onani Zakumapeto A5.
Mʼchilankhulo choyambirira, “mutu wa kona.”
Onani Zakumapeto A5.
Kapena kuti, “kumumanga.”
Kapena kuti, “nʼzoyenera.”
Onani Zakumapeto B14.
Onani Zakumapeto A5.
Onani Zakumapeto A5.
Kapena kuti, “mipando yabwino kwambiri.”
Kapena kuti, “Mphunzitsi.”
Onani Zakumapeto A3.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Kapena kuti, “kulanda zinthu za eni.”
Kapena kuti, “manda achikumbutso.”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mabaibulo ena amati, “nʼkukusiyirani nyumba yanuyi ili bwinja.”
Onani Zakumapeto A5.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Kapena kuti, “chiyambi cha mavuto aakulu ngati ululu umene mzimayi amamva akatsala pangʼono kubereka.”
Kapena kuti, “amene wapirira.”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Kapena kuti, “anzeru.”
Talente imodzi ya Agiriki inali yofanana ndi makilogalamu 20.4. Onani Zakumapeto B14.
Mʼchilankhulo choyambirira, “ndalama ya siliva.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ndalama zasiliva.”
Apa akunena za ana a Adamu ndi Hava.
Kapena kuti, “wosavala mokwanira.”
Kapena kuti, “adzaphedwa.”
Kapena kuti, “amange.”
Kapena kuti, “masalimo.”
Kapena kuti, “Moyo wanga ukumva chisoni.”
Kapena kuti, “malemba akwaniritsidwe.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Sanihedirini.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “magazi osalakwa.”
Kapena kuti, “Amenewo ndi mavuto ako.”
Mawuwa kwenikweni ndi a pa Zek 11:12, 13. Mʼnthawi ya Mateyu, buku la Yeremiya linali loyambirira mumpukutu wa mabuku a aneneri. Choncho mwina mabuku onse a aneneri, kuphatikizapo la Zekariya, ankadziwika kuti Yeremiya. Yerekezani ndi Lu 24:44.
Onani Zakumapeto A5.
Kapena kuti, “Aphedwe popachikidwa pamtengo.”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mʼchilankhulo choyambirira, “ola la 6,” kuwerenga kuchokera mʼma 6 koloko mʼmawa.
Mʼchilankhulo choyambirira, “ola la 9,” kuwerenga kuchokera mʼma 6 koloko mʼmawa.
Kapena kuti, “Manda achikumbutso.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mayi wa ana a Zebedayo.”
Kapena kuti, “mʼmanda achikumbutso.”
Kapena kuti, “manda achikumbutsowo.”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Onani Zakumapeto A5.
Mʼchilankhulo choyambirira, “timunyengerera.”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.