KALATA YOPITA KWA AHEBERI
1 Kalekale, Mulungu ankalankhula ndi makolo athu kudzera mwa aneneri. Anachita zimenezi kambirimbiri ndiponso mʼnjira zosiyanasiyana.+ 2 Kumapeto kwa masiku ano, iye walankhula ndi ife kudzera mwa Mwana wake,+ amene anamusankha kuti akhale wolandira zinthu zonse monga cholowa.+ Komanso kudzera mwa iyeyu, Mulungu anachititsa kuti pakhale nthawi* zosiyanasiyana.+ 3 Iye amasonyeza bwino ulemerero wa Mulungu+ ndipo ndi chithunzi chenicheni cha Mulunguyo.+ Komanso mawu ake amphamvu amathandiza kuti zinthu zikhalepobe. Ndipo atatiyeretsa potichotsera machimo athu,+ anakhala kudzanja lamanja la Wolemekezeka kumwamba.+ 4 Choncho iye wakhala woposa angelo,+ moti dzina limene walandira monga cholowa, ndi lapamwamba kwambiri kuposa lawo.+
5 Mwachitsanzo, kodi Mulungu anauzapo mngelo uti kuti: “Iwe ndiwe mwana wanga. Lero ine ndakhala bambo ako”?+ Komanso kuti: “Ine ndidzakhala bambo ake ndipo iye adzakhala mwana wanga”?+ 6 Koma ponena za nthawi imene adzatumizenso Mwana wake woyamba kubadwayo+ padziko lapansi, iye akuti: “Angelo onse a Mulungu amugwadire.”
7 Ndiponso ponena za angelo, iye akuti: “Amachititsa kuti angelo ake akhale amphamvu* ndipo amachititsa atumiki ake+ kukhala ngati lawi la moto.”+ 8 Koma ponena za Mwana wake, iye akuti: “Mulungu ndi mpando wako wachifumu+ mpaka kalekale ndipo ndodo ya Ufumu wako, ndi ndodo yachilungamo. 9 Unkakonda chilungamo ndipo unkadana ndi kusamvera malamulo. Nʼchifukwa chake Mulungu, Mulungu wako, anakudzoza+ ndi mafuta achisangalalo chachikulu kuposa mafumu anzako.”+ 10 Iye akunenanso kuti: “Ambuye, pachiyambipo munakhazikitsa maziko a dziko lapansi, ndipo kumwamba ndi ntchito ya manja anu. 11 Zinthu zimenezi zidzatha, koma inu mudzakhalapobe. Mofanana ndi chovala, zonsezi zidzatha. 12 Mudzapindapinda zinthu zimenezi ngati mkanjo komanso ngati chovala ndipo zidzasinthidwa. Koma inu simudzasintha, ndipo mudzakhalapo mpaka kalekale.”+
13 Koma kodi ndi mngelo uti amene anamuuzapo kuti: “Khala kudzanja langa lamanja, mpaka nditaika adani ako kuti akhale chopondapo mapazi ako”?+ 14 Angelo onse ndi mizimu yotumikira ena.*+ Mulungu amawatumiza kuti akatumikire omwe iye adzawapulumutse.
2 Nʼchifukwa chake zinthu zimene tinamva tiyenera kuziganizira mozama kuposa nthawi zonse,+ kuti tisatengeke pangʼonopangʼono nʼkusiya chikhulupiriro.+ 2 Chifukwa ngati mawu amene angelo ananena+ analidi oona, ndipo chilango chinaperekedwa mwachilungamo pa tchimo lililonse ndi kusamvera kulikonse,+ 3 ndiye tidzapulumuka bwanji ngati titanyalanyaza chipulumutso chachikulu chonchi?+ Ambuye wathu ndi amene anayamba kunena za chipulumutsochi+ ndipo anthu amene anamumva anatitsimikizira zimenezo. 4 Mulungu nayenso anachitira umboni za chipulumutsochi pogwiritsa ntchito zizindikiro, zinthu zodabwitsa, ntchito zamphamvu zosiyanasiyana+ komanso mzimu woyera umene anaupereka mogwirizana ndi chifuniro chake.+
5 Dziko lapansi limene likubweralo, limene ife tikunena, sanaliike pansi pa ulamuliro wa angelo.+ 6 Koma mboni ina inanena penapake kuti: “Munthu ndi ndani kuti muzimuganizira, kapena mwana wa munthu ndi ndani kuti muzimusamalira?+ 7 Munamutsitsa pangʼono poyerekeza ndi angelo. Munamuveka ulemerero ndi ulemu ngati chisoti chachifumu ndipo munamuika kuti azilamulira ntchito za manja anu. 8 Mwaika zinthu zonse pansi pa mapazi ake.”+ Popeza Mulungu anaika zinthu zonse pansi pa Mwana wake,+ ndiye kuti palibe chilichonse chimene anasiya osachiika pansi pa Mwanayo.+ Komabe, panopa sitikuona kuti zinthu zonse zili pansi pake.+ 9 Koma tikuona Yesu, amene anamutsitsa pangʼono poyerekeza ndi angelo.+ Panopa amuveka ulemerero ndi ulemu ngati chisoti chachifumu chifukwa chakuti anafa.+ Chifukwa cha kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu, zimenezi zinamuchitikira kuti alawe imfa mʼmalo mwa munthu aliyense.+
10 Zinthu zonse zinakhalapo kuti zipereke ulemerero kwa Mulungu komanso zinakhalapo kudzera mwa iye. Choncho kuti athandize ana ambiri kukhala ndi ulemerero,+ zinali zoyenera kuti achititse Mtumiki Wamkulu wachipulumutso chawo+ kukhala wangwiro kudzera mʼmavuto amene anakumana nawo.+ 11 Chifukwa onse, woyeretsa ndi amene ayeretsedwawo,+ amachokera kwa mmodzi.+ Choncho iye sachita manyazi kuwatchula kuti “abale” ake,+ 12 pamene akunena kuti: “Ndidzalengeza dzina lanu kwa abale anga. Ndidzakutamandani poimba nyimbo pakati pa mpingo.”+ 13 Komanso pamene akunena kuti: “Ine ndidzamudalira.”+ Ndiponso kuti: “Taonani! Ine ndi ana amene Yehova* wandipatsa.”+
14 Popeza “ana” onsewo ndi a magazi ndi mnofu, iyenso anakhala wa magazi ndi mnofu.+ Anachita izi kuti kudzera mu imfa yake, awononge Mdyerekezi,+ amene ali ndi njira yobweretsera imfa.+ 15 Anachitanso zimenezi kuti amasule onse amene anali mu ukapolo moyo wawo wonse chifukwa choopa imfa.+ 16 Chifukwa sikuti iye akuthandiza angelo, koma akuthandiza mbadwa* za Abulahamu.+ 17 Choncho iye anayenera kukhala ngati “abale” ake pa zinthu zonse,+ kuti akhale mkulu wa ansembe wachifundo komanso wokhulupirika pa zinthu zokhudza Mulungu, nʼcholinga choti apereke nsembe yophimba machimo a anthu+ kuti tigwirizanenso ndi Mulungu. 18 Popeza iye anavutika pamene ankayesedwa,+ amatha kuthandiza anthu amene akuyesedwa.+
3 Choncho, abale athu oyera, amene muli mʼgulu la anthu oitanidwa kumwamba,+ ganizirani za Yesu, mtumwi ndi mkulu wa ansembe amene tikumuvomereza.+ 2 Iye anali wokhulupirika kwa Mulungu amene anamuika kukhala mtumwi ndi mkulu wa ansembe,+ ngati mmenenso Mose analili wokhulupirika mʼnyumba yonse ya Mulungu.+ 3 Yesu akuyenera kupatsidwa ulemerero waukulu+ kuposa Mose, chifukwa womanga nyumba amakhala wolemekezeka kuposa nyumbayo. 4 Nʼzoona kuti nyumba iliyonse inamangidwa ndi winawake, koma amene anapanga zinthu zonse ndi Mulungu. 5 Mose anali mtumiki wokhulupirika mʼnyumba yonse ya Mulungu ndipo utumiki wakewo unali umboni wa zinthu zimene zidzanenedwe mʼtsogolo. 6 Koma Khristu anali mwana ndipo ankayangʼanira nyumba ya Mulungu mokhulupirika.+ Ife tikhalabe nyumba ya Mulunguyo+ tikapitiriza kukhala ndi ufulu wa kulankhula komanso kugwira mwamphamvu chiyembekezo chimene timachinyadira mpaka mapeto.
7 Choncho mogwirizana ndi zimene mzimu woyera ukunena+ kuti: “Lero mukamva mawu a Mulungu, 8 musaumitse mitima yanu ngati mmene zinakhalira pamene makolo anu anandipsetsa mtima kwambiri, ngati mmene zinalili pa tsiku limene anandiyesa mʼchipululu.+ 9 Mʼchipululumo, makolo anu anandiyesa ngakhale kuti anali ataona ntchito zanga kwa zaka 40.+ 10 Nʼchifukwa chake ndinanyansidwa ndi mʼbadwo umenewo, ndipo ndinati, ‘Mitima yawo imasochera nthawi zonse ndipo njira zanga sakuzidziwa.’ 11 Choncho ndinalumbira nditakwiya kuti, ‘Sadzalowa mumpumulo wanga.’”+
12 Chenjerani abale kuti pakati panu, wina asachoke kwa Mulungu wamoyo nʼkukhala ndi mtima woipa wopanda chikhulupiriro.+ 13 Mʼmalomwake, pitirizani kulimbikitsana tsiku ndi tsiku, nthawi iliyonse imene mukuti “Lero,”+ kuti chinyengo champhamvu cha uchimo chisaumitse mtima wa aliyense wa inu. 14 Chifukwa timachita nawo zimene Khristu akuchita, ngati zinthu zimene tinkadalira poyamba tazigwira mwamphamvu mpaka mapeto.+ 15 Paja Malemba amati: “Lero mukamva mawu a Mulungu, musaumitse mitima yanu ngati mmene zinakhalira pamene makolo anu anandipsetsa mtima kwambiri.”+
16 Kodi paja ndi ndani amene anamva koma nʼkupsetsa mtima Mulungu? Kodi si anthu onse amene anatuluka mʼdziko la Iguputo motsogoleredwa ndi Mose?+ 17 Komanso, kodi Mulungu ananyansidwa ndi ndani kwa zaka 40?+ Kodi si anthu amene anachimwa aja, amene anafera mʼchipululu?+ 18 Nanga kodi analumbirira ndani kuti sadzalowa mumpumulo wake? Kodi si omwe aja amene sanamumvere? 19 Choncho, tikuona kuti sakanatha kulowa mumpumulowo chifukwa anali opanda chikhulupiriro.+
4 Choncho, popeza lonjezo lolowa mumpumulo wake lidakalipo, samalani kuopera kuti wina wa inu angalephere kukwaniritsa zofunika kuti akalowe mu mpumulowo.+ 2 Uthenga wabwino unalengezedwa kwa ife,+ ngati mmenenso anaulengezera kwa makolo athu. Koma mawu amene iwo anamva sanapindule nawo, chifukwa analibe chikhulupiriro chofanana ndi cha amene anamvera mawuwo. 3 Ife amene tasonyeza chikhulupiriro tikulowadi mumpumulowo. Ponena za mpumulo umenewu iye anati: “Choncho ndinalumbira nditakwiya kuti, ‘Sadzalowa mumpumulo wanga,’”+ ngakhale kuti anali atamaliza ntchito zake pa nthawi imene dziko linkakhazikitsidwa.*+ 4 Ponena za tsiku la 7, penapake anati: “Ndipo Mulungu anapuma pa ntchito zake zonse pa tsiku la 7.”+ 5 Panonso akunena kuti: “Sadzalowa mumpumulo wanga.”+
6 Choncho, popeza mwayi wolowa mumpumulowo udakalipo, ndipo amene anali oyamba kumva uthenga wabwino sanalowemo chifukwa cha kusamvera,+ 7 patapita nthawi, Mulungu ananena mu salimo la Davide, ngati mmene tanenera kale mu kalatayi kuti: “Lero anthu inu mukamva mawu a Mulungu, musaumitse mitima yanu.”+ Choncho wapatula tsiku limene akulitchula kuti “Lero.” 8 Chifukwa Yoswa+ akanawalowetsa mʼmalo ampumulo, Mulungu sakananenanso pambuyo pake za tsiku lina. 9 Choncho mpumulo wa sabata udakalipo kwa anthu a Mulungu.+ 10 Munthu amene walowa mumpumulo wa Mulungu, ndiye kuti wapumanso pa ntchito zake, ngati mmene Mulungu anapumira pa ntchito zake.+
11 Choncho, tiyeni tichite zonse zimene tingathe kuti tilowe mumpumulo umenewo, nʼcholinga choti wina asakhale wosamvera ngati makolo athuwo.+ 12 Chifukwa mawu a Mulungu ndi amoyo komanso amphamvu,+ ndipo ndi akuthwa kuposa lupanga lililonse lakuthwa konsekonse.+ Amalasa munthu mumtima mpaka kulekanitsa moyo ndi mzimu komanso mafupa* ndi mafuta amʼmafupa. Mawu a Mulungu amathanso kuzindikira zimene munthu akuganiza komanso zolinga za mtima wake. 13 Palibe cholengedwa chimene Mulungu sangathe kuchiona.+ Chifukwa kwa iye zinthu zonse zili poonekera ndipo amatha kuziona bwinobwino moti ifeyo tidzayankha kwa Mulunguyo pa zochita zathu.+
14 Choncho, popeza tili ndi mkulu wa ansembe wapamwamba, Yesu Mwana wa Mulungu,+ amene anapita kumwamba, tiyeni tipitirize kulengeza zoti timamukhulupirira.+ 15 Chifukwa mkulu wa ansembe amene tili nayeyu, si mkulu wa ansembe amene sangatimvere chisoni pa zofooka zathu.+ Koma ndi mkulu wa ansembe amene anayesedwa pa zinthu zonse ngati ifeyo, ndipo anakhalabe wopanda uchimo.+ 16 Choncho, tiyeni tizifika kumpando wachifumu wa Mulungu ndipo tizipemphera ndi ufulu wa kulankhula+ kuti atichitire chifundo komanso kutisonyeza kukoma mtima kwakukulu pa nthawi yoyenera.
5 Mkulu wa ansembe aliyense wotengedwa pakati pa anthu, amaikidwa kuti azigwira ntchito ya Mulungu mʼmalo mwa anthu,+ kuti azipereka mphatso ndi nsembe zophimba machimo.+ 2 Amakhala woleza mtima pochita zinthu ndi anthu osadziwa kanthu komanso olakwa,* chifukwa iyenso ali ndi zofooka. 3 Ndipo chifukwa cha zimenezo, amafunika kupereka nsembe za machimo ake, ngati mmenenso amaperekera nsembe za machimo a anthu ena.+
4 Munthu samalandira ulemu umenewu mwa kufuna kwake, koma amachita kupatsidwa ndi Mulungu ngati mmene anachitira Aroni.+ 5 Zilinso chimodzimodzi ndi Khristu. Iye sanadzipatse yekha ulemerero+ podziika yekha kukhala mkulu wa ansembe. Koma amene anamupatsa ulemerero umenewo ndi amene anamuuza kuti: “Iwe ndiwe mwana wanga. Lero ine ndakhala bambo ako.”+ 6 Ngatinso mmene akunenera penapake kuti: “Iwe ndiwe wansembe mpaka kalekale, mofanana ndi unsembe wa Melekizedeki.”+
7 Pamene Khristu anali padzikoli,* anapereka mapemphero ochonderera ndiponso opempha, kwa amene akanatha kumupulumutsa ku imfa. Anapereka mapempherowa mofuula komanso akugwetsa misozi,+ ndipo anamumvera chifukwa ankaopa Mulungu. 8 Ngakhale kuti anali Mwana wa Mulungu, anaphunzira kumvera chifukwa cha mavuto amene anakumana nawo.+ 9 Ndipo atakhala wangwiro,+ anali ndi udindo wopulumutsa kwamuyaya anthu onse amene amamumvera,+ 10 chifukwa wasankhidwa ndi Mulungu kuti akhale mkulu wa ansembe mofanana ndi unsembe wa Melekizedeki.+
11 Tili ndi zambiri zoti tinene zokhudza iyeyu, koma zikuvuta kuzifotokoza chifukwa chakuti inu mumachedwa kumvetsa zinthu. 12 Pofika pano munayenera kukhala aphunzitsi. Koma sizili choncho, ndipo mukufunikanso wina woti akuphunzitseni mfundo zoyambirira+ za mʼmawu opatulika a Mulungu, kuyambira pachiyambi. Inu mwayambanso kufuna mkaka, osati chakudya chotafuna. 13 Aliyense amene amangomwabe mkaka sadziwa mawu a chilungamo ndipo adakali kamwana.+ 14 Koma chakudya chotafuna ndi cha anthu aakulu mwauzimu, amene amatha kusiyanitsa zoyenera ndi zosayenera chifukwa choti amagwiritsa ntchito luso lawo la kuganiza.*
6 Choncho popeza tamaliza kuphunzira mfundo zoyambirira+ zokhudza Khristu, tiyeni tiyesetse mwakhama kuti tikhale aakulu mwauzimu.+ Tisayambe kuyalanso maziko, amene ndi kulapa ntchito zakufa, kukhulupirira Mulungu, 2 chiphunzitso chokhudza ubatizo, kuika manja,+ kuuka kwa akufa+ ndiponso chiweruzo chamuyaya. 3 Mulungu akalola, tiyesetsadi kuti tikule mwauzimu.
4 Pali anthu amene Mulungu anawaunikira,+ amene analandirapo mphatso yaulere yakumwamba, amene analandira mzimu woyera 5 komanso amene anamvapo mawu abwino a Mulungu ndi madalitso* amene adzaperekedwe padziko limene likubweralo. 6 Koma tsopano anthu amenewa anagwa+ ndipo nʼzosatheka kuwadzutsanso kuti alape, chifukwa akupachika kachiwiri Mwana wa Mulungu ndiponso kumunyoza poyera.+ 7 Nthaka imalandira madalitso kuchokera kwa Mulungu ikamwa madzi a mvula imene imagwera panthakapo kawirikawiri. Kenako imatulutsa zomera zimene zimathandiza amene ailima. 8 Koma ikatulutsa minga ndi zitsamba zobaya, imakanidwa ndipo imatsala pangʼono kutembereredwa. Mapeto ake imatenthedwa.
9 Koma ngakhale kuti tikulankhula chonchi, sitikukayikira kuti pa nkhani ya zinthu zobweretsa chipulumutso, inu okondedwa muli pabwino kusiyana ndi amene anagwa aja. 10 Chifukwa Mulungu si wosalungama kuti angaiwale ntchito yanu ndiponso chikondi chimene munachisonyeza pa dzina lake,+ potumikira oyera ndipo mukupitiriza kuwatumikira. 11 Koma tikufuna kuti nonsenu mupitirize kusonyeza khama limene munali nalo poyamba, kuti chiyembekezo chanu chikhale chotsimikizika+ mpaka mapeto.+ 12 Muchite zimenezi kuti musakhale aulesi,+ koma muzitsanzira anthu amene, chifukwa cha chikhulupiriro ndiponso kuleza mtima, akulandira zinthu zimene Mulungu analonjeza.
13 Pamene Mulungu analonjeza Abulahamu, analumbira pa dzina lake chifukwa panalibe wina wamkulu kuposa iyeyo amene akanamulumbirira.+ 14 Iye anati: “Ndithudi ndidzakudalitsa ndipo ndidzachulukitsa mbadwa zako.”+ 15 Choncho Abulahamu atasonyeza kuleza mtima, analandira lonjezo limeneli. 16 Chifukwa anthu polumbira amatchula winawake wamkulu kuposa iwowo, ndipo lumbiro lawo limathetsa mkangano uliwonse chifukwa lumbirolo limatsimikizira mwalamulo zomwe munthu wanena.+ 17 Mofanana ndi zimenezi, Mulungu anafuna kutsimikizira anthu olandira lonjezolo+ kuti chifuniro chake sichingasinthe. Choncho anachita kulumbira pa zimene analonjezazo. 18 Anachita zimenezo kuti pa zinthu ziwiri zosasinthika, zomwe chifukwa cha zimenezi nʼzosatheka kuti Mulungu aname,+ ife amene tathawira kumalo otetezeka tilimbikitsidwe nʼkumakhulupirira kwambiri* zinthu zimene tikuyembekezera. 19 Chiyembekezo chathuchi+ chili ngati nangula* wa miyoyo yathu ndipo nʼchotsimikizika komanso chokhazikika. Chiyembekezochi chimatilowetsa mkati, kuseri kwa katani yotchingira+ 20 kumene Yesu, yemwe ndi kalambulabwalo, anakalowa chifukwa cha ife.+ Iyeyu ndi mkulu wa ansembe mpaka kalekale mofanana ndi unsembe wa Melekizedeki.+
7 Melekizedeki ameneyu anali mfumu ya mzinda wa Salemu komanso wansembe wa Mulungu Wamʼmwambamwamba, ndipo anachingamira Abulahamu pochokera kokapha mafumu nʼkumudalitsa.+ 2 Abulahamu anamupatsa chakhumi cha zinthu zonse. Dzina lakeli limamasuliridwa kuti “Mfumu Yachilungamo” komanso mfumu ya Salemu, kutanthauza “Mfumu Yamtendere.” 3 Popeza analibe bambo, analibe mayi, analibe mzere wa makolo ndipo tsiku limene anabadwa komanso limene anamwalira silikudziwika, koma anamuchititsa kuti afanane ndi Mwana wa Mulungu, iye ndi wansembe mpaka kalekale.+
4 Choncho mungaone kuti munthuyu anali wofunika kwambiri. Moti kholo lathu Abulahamu, anamupatsa chakhumi pa zinthu zabwino kwambiri zimene anatenga kunkhondo.+ 5 Zoonadi mogwirizana ndi Chilamulo, ana aamuna a Levi+ amene amapatsidwa udindo wa unsembe, analamulidwa kuti azilandira zakhumi kuchokera kwa anthu.+ Anthu amenewa anali abale awo ngakhale kuti abale awowo anali mbadwa za Abulahamu. 6 Koma munthu ameneyu, yemwe sanachokere mumzere wobadwira wa Levi analandira chakhumi kuchokera kwa Abulahamu, ndipo anadalitsa Abulahamuyo amene analandira malonjezo kuchokera kwa Mulungu.+ 7 Choncho palibe angatsutse kuti wamngʼono anadalitsidwa ndi wamkulu. 8 Alevi ankalandira zakhumi ndipo ndi anthu oti amafa. Koma munthu wina amene analandira zakhumi, Malemba amamuchitira umboni kuti ali moyo.+ 9 Tikhozanso kunena kuti ngakhalenso Levi amene amalandira zakhumi anapereka zakhumi kudzera mwa Abulahamu. 10 Chifukwa Levi anali asanabadwe pamene kholo lake Abulahamu anakumana ndi Melekizedeki, koma anali woti adzakhala mbadwa ya Abulahamuyo.+
11 Kukhala ndi ansembe a fuko la Levi kunali mbali ya Chilamulo cha Mose chimene Aisiraeli anapatsidwa. Ndiye zikanakhala kuti ansembe a fuko la Levi angathandize anthu kukhala angwiro,+ kodi pakanafunikanso wansembe ngati Melekizedeki?+ Kodi sizikanakhala zokwanira kungokhala ndi wansembe ngati Aroni? 12 Popeza kuti unsembewo ukusinthidwa, ndiye kuti Chilamulonso chifunika kusintha.+ 13 Munthu amene akufotokozedwa pamenepa ndi wa fuko lina ndipo palibe aliyense wa fuko limenelo amene anatumikirapo paguwa lansembe.+ 14 Tonse tikudziwa kuti Ambuye wathu anachokera ku fuko la Yuda+ koma Mose sananenepo kuti ansembe adzachokera mu fuko limeneli.
15 Zimenezi zikumveka bwino tsopano chifukwa pabwera wansembe wina+ wofanana ndi Melekizedeki.+ 16 Iyeyu wakhala wansembe, osati mogwirizana ndi malamulo, amene amadalira zinthu zapadziko lapansi, koma mogwirizana ndi mphamvu ya moyo umene sungawonongeke.+ 17 Chifukwa Malemba anamuchitira umboni kuti: “Iwe ndiwe wansembe mpaka kalekale mofanana ndi unsembe wa Melekizedeki.”+
18 Choncho malamulo oyambawo akuchotsedwa chifukwa ndi operewera komanso osathandiza.+ 19 Chilamulo sichinapangitse chilichonse kukhala changwiro.+ Koma chiyembekezo cha zinthu zabwino chimene anabweretsa,+ chomwe chikutithandiza kuyandikira Mulungu,+ chinachita zimenezi. 20 Komanso zimenezi sizinachitike popanda lumbiro. 21 (Chifukwa pali amuna ena amene akhala ansembe popanda lumbiro, koma ameneyu wakhala wansembe pochita kumulumbirira. Lumbiro limeneli ndi la amene ananena za wansembeyo kuti: “Yehova* walumbira kuti, ‘Iwe ndiwe wansembe mpaka kalekale,’ ndipo sadzasintha maganizo.”)+ 22 Mogwirizana ndi zimenezi, Yesu wakhala chikole cha pangano labwino kwambiri.+ 23 Ndiponso pankafunika ansembe ambiri olowa mʼmalo+ chifukwa imfa inkachititsa kuti munthu asapitirize kukhala wansembe. 24 Koma popeza iye adzakhala ndi moyo mpaka kalekale,+ palibe wansembe amene adzamulowe mʼmalo. 25 Choncho akhoza kupulumutsa anthu amene akupemphera kwa Mulungu mʼdzina lake, chifukwa iye sadzafa ndipo aziwachonderera kwa Mulungu.+
26 Mkulu wa ansembe ngati ameneyu ndi wotiyeneradi chifukwa ndi wokhulupirika, wosalakwa, wosaipitsidwa,+ wosiyana ndi anthu ochimwa ndipo wakwezedwa pamwamba kwambiri.+ 27 Mosiyana ndi akulu a ansembe ena, iye safunikira kupereka tsiku ndi tsiku nsembe+ za machimo ake choyamba, kenako za anthu ena.+ Zili choncho chifukwa iye anadzipereka kamodzi kokha kuti akhale nsembe yothandiza anthu mpaka kalekale.+ 28 Chilamulo chimaika amuna okhala ndi zofooka kukhala akulu a ansembe.+ Koma mawu a lumbiro+ amene ananenedwa pambuyo pa Chilamulo anaika Mwana, amene anakhala wangwiro+ mpaka kalekale.
8 Pa zimene tikunenazi, mfundo yaikulu ndi yakuti: Tili ndi mkulu wa ansembe ngati ameneyu,+ ndipo iye wakhala kudzanja lamanja la mpando wachifumu wa Wolemekezeka kumwamba.+ 2 Iye ndi mtumiki wamʼmalo oyerawo+ komanso mʼchihema chenicheni, chomangidwa ndi Yehova* osati munthu. 3 Mkulu wa ansembe aliyense amaikidwa kuti azipereka mphatso ndiponso nsembe. Choncho uyunso anafunika kukhala ndi chinachake choti apereke.+ 4 Iye akanakhalabe padziko lapansi sakanakhala wansembe,+ chifukwa pali kale amuna opereka mphatsozo malinga ndi Chilamulo. 5 Utumiki umene amuna amenewa akuchita uli ngati chifaniziro ndiponso chithunzi+ cha zinthu zakumwamba.+ Izi zikufanana ndi lamulo limene Mulungu anapatsa Mose atatsala pangʼono kumanga chihema. Lamulo lake linali lakuti: “Uonetsetse kuti wapanga zinthu zonse motsatira chitsanzo chimene wasonyezedwa mʼphiri.”+ 6 Koma Yesu walandira utumiki wapamwamba kwambiri, chifukwa iyenso ndi mkhalapakati+ wa pangano labwino kwambiri,+ limene lakhazikitsidwa mwalamulo pa malonjezo abwinonso.+
7 Pangano loyamba lija likanakhala lopanda zolakwika, sipakanafunikanso pangano lachiwiri.+ 8 Chifukwa Mulungu akuona kuti anthu akulakwitsa zinazake choncho iye akunena kuti: “‘Taonani! Masiku akubwera pamene ndidzachita pangano latsopano ndi nyumba ya Isiraeli komanso ndi nyumba ya Yuda,’ akutero Yehova.* 9 ‘Koma silidzakhala pangano lofanana ndi limene ndinachita ndi makolo awo pa tsiku limene ndinagwira dzanja lawo kuti ndiwatulutse mʼdziko la Iguputo.+ Popeza sanapitirize kusunga pangano langalo, ndinasiya kuwasamalira,’ akutero Yehova.”*
10 “‘Pangano limene ndidzapangane ndi nyumba ya Isiraeli pambuyo pa masiku amenewo ndi ili: Ndidzaika malamulo anga mʼmaganizo mwawo ndiponso kuwalemba mʼmitima yawo.+ Ine ndidzakhala Mulungu wawo ndipo iwo adzakhala anthu anga,’+ akutero Yehova.*
11 ‘Munthu sadzaphunzitsanso nzika inzake kapena mʼbale wake kuti, “Mumʼdziwe Yehova!”* Chifukwa aliyense adzandidziwa kuyambira wamngʼono mpaka wamkulu. 12 Ine ndidzawachitira chifundo pa zochita zawo zosalungama, ndipo sindidzakumbukiranso machimo awo.’”+
13 Ponena kuti “pangano latsopano,” iye wachititsa kuti loyambalo lithe ntchito.+ Pangano limene latha ntchito ndipo likukalamba, ndiye kuti latsala pangʼono kufafanizika.+
9 Pangano loyamba lija linali ndi malamulo ake a utumiki wopatulika ndiponso malo ake oyera+ apadziko lapansi. 2 Chifukwa panamangidwa chipinda choyamba cha chihema ndipo mʼchipindamo munali choikapo nyale,+ tebulo ndi mikate yoonetsa kwa Mulungu,*+ ndipo chinkatchedwa “Malo Oyera.”+ 3 Koma kuseri kwa nsalu yotchinga yachiwiri+ kunali chipinda chinanso chotchedwa “Malo Oyera Koposa.”+ 4 Mmenemu munali chiwaya chagolide chofukizira nsembe+ ndi likasa la pangano+ lokutidwa ndi golide.+ Mulikasamo munali mtsuko wagolide wokhala ndi mana,+ ndodo ya Aroni imene inaphuka ija+ komanso miyala yosema+ ya pangano. 5 Pamwamba pa likasalo panali akerubi aulemerero amene zithunzithunzi zawo zinkafika pachivundikiro.*+ Koma ino si nthawi yofotokoza zinthu zimenezi mwatsatanetsatane.
6 Zinthu zimenezi zitakonzedwa chonchi, nthawi ndi nthawi ansembe ankalowa mʼchipinda choyamba kukachita mautumiki opatulika.+ 7 Koma mʼchipinda chachiwiricho, mkulu wa ansembe yekha ndi amene ankalowamo kamodzi pa chaka,+ ndipo sankalowa popanda kutenga magazi.+ Magaziwo ankawapereka chifukwa cha iyeyo,+ komanso chifukwa cha machimo a anthu+ amene anawachita mosadziwa. 8 Choncho mzimu woyera umatithandiza kumvetsa bwino kuti njira yolowera kumalo oyera inali isanaonekere pamene chihema choyambacho chinalipo.+ 9 Chihema chimenecho chinali chifaniziro cha nthawi inoyo+ ndipo mogwirizana ndi chifanizirocho, mphatso ndiponso nsembe zimaperekedwa.+ Komabe, zimenezi sizipangitsa munthu amene akuchita utumiki wopatulikayo kukhala ndi chikumbumtima choyera.+ 10 Mʼmalomwake, zimangokhudza zakudya, zakumwa ndi miyambo yosiyanasiyana yoyeretsa zinthu ndi madzi.*+ Zimenezo zinali zofunika mogwirizana ndi malamulo okhudza thupi+ ndipo anazikhazikitsa mpaka nthawi yokonzanso zinthu.
11 Komabe, pamene Khristu anabwera monga mkulu wa ansembe wa zinthu zabwino zimene zakwaniritsidwa, anadzera mʼchihema chachikulu ndi changwiro kwambiri chimene sichinapangidwe ndi manja a anthu, kutanthauza kuti sichipezeka padzikoli. 12 Iye analowa mʼmalo oyera ndi magazi ake,+ osati ndi magazi a mbuzi kapena a ngʼombe zazingʼono zamphongo. Analowa kamodzi kokha mʼmalo oyerawo ndipo anatipulumutsa kwamuyaya.+ 13 Chifukwa ngati magazi a mbuzi ndi a ngʼombe zamphongo+ komanso phulusa la ngʼombe yaikazi,* zimene amawaza nazo anthu odetsedwa, zimawayeretsa mpaka kukhaladi oyera pamaso pa Mulungu,+ 14 kuli bwanji magazi a Khristu,+ amene anadzipereka wopanda chilema kwa Mulungu kudzera mwa mzimu woyera?* Kodi magazi amenewo sadzayeretsa zikumbumtima zathu ku ntchito zakufa,+ kuti tichite utumiki wopatulika kwa Mulungu wamoyo?+
15 Ndiye chifukwa chake iye ndi mkhalapakati wa pangano latsopano+ kuti anthu amene aitanidwa alandire lonjezo la moyo wosatha.+ Izi zatheka chifukwa cha imfa yake, imene inali ngati dipo lowamasula+ ku machimo amene iwo anali nawo mʼpangano lakale lija. 16 Pamene pali pangano, pamafunikanso kuti munthu wochita naye panganoyo afe. 17 Chifukwa pangano limagwira ntchito ngati wina wafapo, popeza siligwira ntchito ngati munthu wochita naye panganoyo ali ndi moyo. 18 Ndiye chifukwa chake ngakhale pangano loyamba lija silinakhazikitsidwe popanda magazi. 19 Mose akauza anthu onsewo lamulo lililonse la mʼChilamulo, ankatenga magazi a ngʼombe zazingʼono zamphongo, magazi a mbuzi ndiponso madzi nʼkuwaza bukulo* ndi anthu onse pogwiritsa ntchito ubweya wa nkhosa wofiira kwambiri ndi timitengo ta hisope. 20 Iye ankawauza kuti: “Awa ndi magazi a pangano limene Mulungu wakulamulani kuti mulisunge.”+ 21 Ndipo anawazanso magazi aja pachihema ndi ziwiya zonse zogwiritsa ntchito pa utumiki wopatulika.+ 22 Mogwirizana ndi Chilamulo, pafupifupi zinthu zonse zimayeretsedwa ndi magazi+ ndipo popanda kukhetsa magazi anthu sangakhululukidwe machimo awo.+
23 Choncho zinali zofunika kuti zifaniziro+ za zinthu zakumwamba ziyeretsedwe mʼnjira imeneyi.+ Koma zinthu zakumwamba zenizenizo zimafunika kuyeretsedwa ndi nsembe zabwino kuposa zimenezi. 24 Khristu sanalowe mʼmalo oyera opangidwa ndi manja a anthu,+ amene ndi chithunzi cha malo enieniwo,+ koma analowa kumwamba kwenikweniko.+ Panopa iye ali kumwamba kuti azionekera pamaso pa Mulungu mʼmalo mwa ifeyo.+ 25 Iye sanapite kumwambako kuti azikadzipereka nsembe mobwerezabwereza, ngati mmene mkulu wa ansembe amachitira. Paja mkulu wa ansembe amalowa mʼmalo oyera chaka ndi chaka+ atatenga magazi a nyama, osati ake. 26 Zikanatero, akanavutika mobwerezabwereza kuyambira pamene dziko linakhazikitsidwa. Koma tsopano iye waonekera kamodzi kokha pamapeto a nthawi* ino kuti achotse uchimo kudzera mu nsembe yake.+ 27 Mofanana ndi zimene zimachitikira anthu kuti amayembekezera kufa kamodzi kokha, kenako nʼkudzalandira chiweruzo, 28 nayenso Khristu anaperekedwa nsembe kamodzi kokha kuti anyamule machimo a anthu ambiri.+ Nthawi yachiwiri imene adzaonekere sadzaonekera nʼcholinga chochotsa uchimo. Ndipo amene adzamuone ndi anthu amene akumuyembekezera ndi mtima wonse kuti awapulumutse.+
10 Popeza Chilamulo chimangochitira chithunzi+ zinthu zabwino zimene zikubwera+ ndipo si zinthu zenizenizo, sichingachititse* amene amalambira Mulungu kukhala angwiro pogwiritsa ntchito nsembe zimene amapereka mosalekeza chaka chilichonse.+ 2 Zikanakhala choncho, kodi nsembezo sakanasiya kuzipereka? Akanasiya chifukwa zikanakhala kuti anthu ochita utumiki wopatulikawo ayeretsedwa, sakanakhalanso ndi chikumbumtima chakuti ndi ochimwa. 3 Koma mosiyana ndi zimenezo, chaka chilichonse nsembe zimenezi zimawakumbutsa za machimo awo.+ 4 Chifukwa nʼzosatheka kuti magazi a ngʼombe zamphongo ndi mbuzi achotseretu machimo.
5 Choncho atabwera padzikoli iye anati: “‘Nsembe zanyama komanso nsembe zina simunazifune, koma munandikonzera thupi. 6 Nsembe zopsereza zathunthu ndi nsembe zamachimo simunazivomereze.’+ 7 Ndiyeno ine ndinati, ‘Taonani! Ine ndabwera (mumpukutu munalembedwa za ine) kudzachita chifuniro chanu, inu Mulungu wanga.’”+ 8 Atanena kuti: “Nsembe zanyama, nsembe zopsereza zathunthu, nsembe zamachimo ndiponso nsembe zina simunazifune kapena kuzivomereza,” zomwe ndi nsembe zoperekedwa mogwirizana ndi Chilamulo. 9 Ananenanso kuti: “Taonani! Ine ndabwera kudzachita chifuniro chanu.”+ Akuchotsa dongosolo loyambalo kuti akhazikitse lachiwiri. 10 Tayeretsedwa ndi “chifuniro” chimenecho,+ kudzera mʼthupi la Yesu Khristu limene analipereka nsembe kamodzi kokha.+
11 Komanso, wansembe aliyense amaima pamalo ake kuti achite utumiki wopatulika+ ndiponso kuti apereke nsembe zimodzimodzizo mobwerezabwereza,+ zimene sizingachotseretu machimo.+ 12 Koma munthu ameneyu anapereka nsembe imodzi yamachimo yothandiza mpaka kalekale, ndipo anakhala kudzanja lamanja la Mulungu.+ 13 Kuyambira nthawi imeneyo, akudikira mpaka pamene adani ake adzaikidwe kuti akhale chopondapo mapazi ake.+ 14 Kudzera mu nsembe imodzi yokha, iye akuchititsa anthu amene akuyeretsedwa kukhala angwiro+ mpaka kalekale. 15 Nawonso mzimu woyera ukuchitira umboni kwa ife, chifukwa unanena kuti: 16 “‘Pangano limene ndidzapangane nawo pambuyo pa masiku amenewo ndi ili: Ndidzaika malamulo anga mʼmitima yawo ndipo ndidzawalemba mʼmaganizo awo,’+ akutero Yehova.”* 17 Kenako unanenanso kuti: “Ndipo sindidzakumbukiranso machimo awo komanso zochita zawo zosonyeza kusamvera malamulo.”+ 18 Ndiyeno zimenezi zikakhululukidwa, nsembe yamachimo sikhalanso yofunika.
19 Choncho abale, timalimba mtima kulowa mʼmalo oyera+ chifukwa cha magazi a Yesu. 20 Iye ndi amene anatitsegulira njira imeneyi yomwe ndi yatsopano komanso yamoyo ndipo imadutsa katani yotchingira,+ imene ndi thupi lake. 21 Popeza tili ndi wansembe wamkulu kwambiri woyangʼanira nyumba ya Mulungu,+ 22 tiyeni tifike kwa Mulungu ndi mtima wonse komanso tili ndi chikhulupiriro chonse, chifukwa mitima yathu yayeretsedwa* kuti tisakhalenso ndi chikumbumtima choipa,+ ndipo matupi athu asambitsidwa mʼmadzi oyera.+ 23 Tiyeni tipitirize kulengeza poyera chiyembekezo chathu ndipo tisagwedezeke,+ chifukwa amene watilonjeza ndi wokhulupirika. 24 Ndipo tiyeni tiganizirane* kuti tilimbikitsane pa nkhani yosonyezana chikondi ndiponso kuchita zabwino.+ 25 Tisasiye kusonkhana pamodzi,+ ngati mmene ena achizolowezi chosafika pamisonkhano akuchitira. Koma tiyeni tilimbikitsane+ ndipo tizichita zimenezi kwambiri, makamaka panopa pamene mukuona kuti tsikulo likuyandikira.+
26 Ngati tikuchita machimo mwadala pambuyo podziwa choonadi molondola,+ palibenso nsembe ina imene ingaperekedwe chifukwa cha machimo athuwo.+ 27 Koma pali chiyembekezo china choopsa cha chiweruzo, ndiponso mkwiyo woyaka moto umene udzawononge otsutsawo.+ 28 Munthu aliyense amene wanyalanyaza Chilamulo cha Mose amafa popanda kumuchitira chifundo, ngati anthu awiri kapena atatu apereka umboni.+ 29 Ndiye kuli bwanji munthu amene wapondaponda Mwana wa Mulungu, amene akuona magazi a pangano amene anayeretsedwa nawo ngati chinthu wamba,+ amenenso wanyoza mzimu umene Mulungu amasonyezera kukoma mtima kwakukulu?+ Munthu ameneyu akuyenera kulandira chilango chachikulu kwambiri. 30 Popeza tikumudziwa amene anati: “Kubwezera ndi kwanga, ndidzabwezera ndine.” Amenenso anati: “Yehova* adzaweruza anthu ake.”+ 31 Kupatsidwa chilango ndi Mulungu wamoyo nʼkoopsa.
32 Komabe, pitirizani kukumbukira masiku akale. Paja mutalandira kuwala kochokera kwa Mulungu,+ munakumana ndi mavuto aakulu. 33 Nthawi zina munkanyozedwa ndiponso kuzunzidwa pagulu* ndipo nthawi zina munkathandiza anthu ena amene ankakumana ndi mavuto ngati amenewa. 34 Munkachitira chifundo anthu amene anali mʼndende, ndipo munkasangalalabe ngakhale katundu wanu akulandidwa,+ podziwa kuti muli ndi chuma chabwino kwambiri ndiponso chokhalitsa.+
35 Choncho, musasiye kukhala olimba mtima* chifukwa mudzalandira mphoto yaikulu kwambiri.+ 36 Mukufunika kukhala opirira+ komanso kuchita chifuniro cha Mulungu kuti mudzalandire zimene Mulunguyo walonjeza. 37 “Kwatsala kanthawi kochepa”+ ndipo “amene akubwerayo afika ndithu, sachedwa.”+ 38 “Koma wolungama wanga adzakhala ndi moyo chifukwa cha chikhulupiriro chake,”+ ndipo “ngati angabwerere mʼmbuyo, ine sindikondwera naye.”+ 39 Ife sitili mʼgulu la anthu obwerera mʼmbuyo kupita kuchiwonongeko,+ koma ndife anthu okhala ndi chikhulupiriro chomwe chingatithandize kudzapeza moyo.
11 Chikhulupiriro ndi kusakayikira kuti zimene ukuyembekezera zidzachitika,+ umboni wooneka wakuti zinthu zosaoneka zilipodi. 2 Chifukwa cha chikhulupiriro, anthu akale* anali ndi umboni wakuti Mulungu akusangalala nawo.
3 Chifukwa cha chikhulupiriro, timazindikira kuti mawu a Mulungu anachititsa kuti nthawi* zosiyanasiyana zikhale mʼmalo mwake, moti zinthu zooneka zakhalapo kuchokera ku zinthu zosaoneka.
4 Chifukwa cha chikhulupiriro, Abele anapereka kwa Mulungu nsembe yamtengo wapatali kuposa ya Kaini.+ Ndipo chifukwa cha chikhulupirirocho, Mulungu anamupatsa umboni wakuti anali wolungama chifukwa analandira* mphatso zakezo.+ Ngakhale kuti anafa, iye akulankhulabe+ kudzera mʼchikhulupiriro chakecho.
5 Chifukwa cha chikhulupiriro, Inoki+ anasamutsidwa kuti asafe mozunzika, moti sanapezeke kulikonse chifukwa Mulungu anamusamutsa.+ Asanamusamutse, Mulungu anamupatsa umboni wakuti akusangalala naye. 6 Ndiponso, popanda chikhulupiriro nʼzosatheka kusangalatsa Mulungu. Chifukwa aliyense wofuna kulambira Mulungu ayenera kukhulupirira kuti iye alikodi ndipo amapereka mphoto kwa anthu amene amamufunafuna ndi mtima wonse.+
7 Chifukwa cha chikhulupiriro, Nowa+ atachenjezedwa ndi Mulungu za zinthu zimene zinali zisanaoneke,+ anasonyeza kuopa Mulungu ndipo anamanga chingalawa+ kuti banja lake lipulumukiremo. Chifukwa cha chikhulupiriro, anatsutsa dziko+ ndipo anaonedwa kuti ndi wolungama chifukwa cha chikhulupirirocho.
8 Chifukwa cha chikhulupiriro, Abulahamu+ ataitanidwa, anamvera nʼkupita kumalo amene ankayembekezera kuwalandira ngati cholowa. Iye anapitadi, ngakhale kuti sankadziwa kumene akupita.+ 9 Chifukwa cha chikhulupiriro, ankakhala monga mlendo mʼdziko limene analonjezedwa.+ Iye ankakhala mʼmatenti+ pamodzi ndi Isaki ndi Yakobo, amenenso Mulungu anawalonjeza kuti adzawapatsa dzikoli.+ 10 Chifukwa ankayembekezera mzinda wokhala ndi maziko enieni, mzinda umene wokonza mapulani ake ndiponso kuumanga ndi Mulungu.+
11 Chifukwa cha chikhulupiriro, Sara nayenso analandira mphamvu yokhala ndi pakati* ngakhale kuti anali atapitirira zaka zobereka,+ chifukwa ankaona kuti wolonjezayo ndi wokhulupirika.* 12 Pa chifukwa chimenechi, kuchokera kwa mwamuna mmodzi, amene anali ngati wakufa,+ kunabadwa ana ambirimbiri+ ngati nyenyezi zakumwamba komanso osawerengeka ngati mchenga wa mʼmbali mwa nyanja.+
13 Onsewa anafa ali ndi chikhulupiriro, ngakhale kuti malonjezowo sanakwaniritsidwe pa nthawi yawo.+ Koma anawaona ali patali+ ndipo anawalandira. Analengezanso poyera kuti iwo anali alendo komanso anthu osakhalitsa mʼdzikolo. 14 Chifukwa anthu amene amalengeza zinthu zimenezi amapereka umboni wakuti akufunafuna mwakhama malo awoawo. 15 Koma akanakhala kuti ankangoganizira za kumene anachokera,+ akanapeza chifukwa chowapangitsa kuti abwerere. 16 Koma tsopano akufunitsitsa malo abwino kwambiri, amene ndi akumwamba. Choncho Mulungu sachita manyazi kutchulidwa kuti Mulungu wawo,+ ndipo wawakonzera mzinda.+
17 Chifukwa cha chikhulupiriro, pamene Abulahamu anayesedwa,+ zinali ngati wapereka kale Isaki nsembe. Choncho munthu amene analandira malonjezo mokondwerayu, anali wokonzeka kupereka nsembe mwana wake yemwe anali mmodzi yekha.+ 18 Anali wokonzeka kuchita zimenezo ngakhale kuti anali atauzidwa kuti: “Mbadwa* zimene ndinakulonjeza zidzachokera mwa Isaki.”+ 19 Koma ankadziwa kuti akafa, Mulungu ali ndi mphamvu zomuukitsa. Moti Mulungu anamubwezeradi mwana wakeyo ndipo zimenezi zinkaimira zinthu zina zamʼtsogolo.+
20 Chifukwa cha chikhulupiriro, Isaki nayenso anadalitsa Yakobo+ ndi Esau,+ ndipo anawauza zimene zidzachitike mʼtsogolo.
21 Chifukwa cha chikhulupiriro, Yakobo atatsala pangʼono kumwalira,+ anadalitsa ana aamuna a Yosefe mmodzimmodzi,+ ndipo kenako analambira Mulungu atatsamira ndodo yake.+
22 Chifukwa cha chikhulupiriro, Yosefe atatsala pangʼono kufa, ananena za kusamuka kwa Aisiraeli, ndipo anapereka malangizo okhudza* mafupa ake.*+
23 Chifukwa cha chikhulupiriro, Mose atabadwa, makolo ake anamubisa kwa miyezi itatu,+ chifukwa anaona kuti mwanayo anali wooneka bwino.+ Iwo sanaope lamulo la mfumu.+ 24 Chifukwa cha chikhulupiriro, Mose atakula+ anakana kutchedwa mwana wa mwana wamkazi wa Farao,+ 25 ndipo anasankha kuzunzidwa limodzi ndi anthu a Mulungu, mʼmalo mochita machimo nʼkusangalala kwa nthawi yochepa. 26 Iye anachita zimenezi chifukwa ankaona kuti kunyozedwa kwake monga Wodzozedwa* kuli ngati chuma chamtengo wapatali kuposa chuma cha ku Iguputo, chifukwa ankaganizira kwambiri mphoto imene adzalandire. 27 Chifukwa cha chikhulupiriro anachoka ku Iguputo,+ koma osati chifukwa choopa mfumu.+ Iye anapitiriza kupirira moleza mtima ngati akuona Wosaonekayo.+ 28 Chifukwa cha chikhulupiriro, iye anachita Pasika ndipo anawaza magazi pamafelemu kuti mngelo wa Mulungu asaphe ana awo oyamba kubadwa.+
29 Chifukwa cha chikhulupiriro, anthu a Mulunguwo anawoloka pa Nyanja Yofiira patauma ngati pamtunda,+ koma Aiguputo atayesa kudutsa, nyanjayo inawamiza.+
30 Chifukwa cha chikhulupiriro, mpanda wa Yeriko unagwa, anthu atayenda mouzungulira kwa masiku 7.+ 31 Chifukwa cha chikhulupiriro, Rahabi amene anali hule uja sanaphedwe limodzi ndi anthu osamvera, chifukwa iye analandira mwamtendere anthu amene anakafufuza za mzindawo.+
32 Kodi ndiperekenso zitsanzo zina? Nthawi indichepera kuti ndipitirize kufotokoza za Gidiyoni,+ Baraki,+ Samisoni,+ Yefita,+ Davide+ komanso Samueli+ ndi aneneri ena. 33 Chifukwa cha chikhulupiriro, anthu amenewa anagonjetsa maufumu pankhondo,+ anachita chilungamo, analonjezedwa zinthu zina+ ndiponso anatseka mikango pakamwa.+ 34 Sanapse ndi moto,+ sanaphedwe ndi lupanga,+ anali ofooka koma anapatsidwa mphamvu,+ anamenya nkhondo mwamphamvu+ ndiponso anathamangitsa magulu ankhondo.+ 35 Akazi analandira anthu akufa amene anaukitsidwa.+ Koma anthu ena anazunzidwa chifukwa sanalole kusiya chikhulupiriro chawo kuti amasulidwe. Iwo anachita zimenezi kuti adzaukitsidwe pa kuuka kwabwino kwambiri. 36 Ena anakumana ndi mayesero chifukwa ananyozedwa komanso kukwapulidwa. Kuwonjezera pamenepo anamangidwa+ ndiponso kutsekeredwa mʼndende.+ 37 Anaponyedwa miyala,+ anayesedwa, anadulidwa pakati, anaphedwa ndi lupanga+ ndiponso anayendayenda atavala zikopa za nkhosa ndi zikopa za mbuzi.+ Ankasowa zinthu, ankazunzidwa+ komanso ankakumana ndi mavuto ena.+ 38 Iwo anali abwino kwambiri, osayenera kukhala mʼdziko lotereli. Anayendayenda mʼzipululu, mʼmapiri, mʼmapanga+ ndi mʼmaenje a dziko lapansi.
39 Komabe ngakhale kuti onsewa Mulungu anawapatsa umboni wakuti akusangalala nawo chifukwa cha chikhulupiriro chawo, sanaone kukwaniritsidwa kwa lonjezolo. 40 Zili choncho chifukwa Mulungu anaoneratu chinthu chabwino kwambiri choti atipatse,+ kuti iwo asakhale angwiro popanda ife.
12 Choncho, popeza tazunguliridwa ndi gulu lalikulu chonchi la mboni,* tiyeninso titaye cholemera chilichonse ndi tchimo limene limatikola mosavuta.+ Ndipo tithamange mopirira mpikisano umene talowawu.+ 2 Tichite zimenezi pamene tikuyangʼanitsitsa Mtumiki Wamkulu ndi Wokwaniritsa chikhulupiriro chathu, Yesu.+ Chifukwa chodziwa kuti adzasangalala mʼtsogolo, anapirira mtengo wozunzikirapo.* Iye sanasamale kuti zochititsa manyazi zimuchitikira ndipo panopa wakhala kudzanja lamanja la mpando wachifumu wa Mulungu.+ 3 Choncho ganizirani mozama za munthu amene anapirira malankhulidwe onyoza amenewo a anthu ochimwa,+ amene polankhula zimenezo ankangodzivulaza okha. Ganizirani za munthu ameneyu kuti musatope nʼkutaya mtima.+
4 Polimbana ndi tchimoli, sikuti mwamenya nkhondo mpaka kufika potaya magazi anu. 5 Ndipo mwaiwaliratu malangizo okudandaulirani ngati amene bambo amauza ana ake kuti: “Mwana wanga, usapeputse chilango* cha Yehova,* kapena kutaya mtima pamene iye akukudzudzula. 6 Chifukwa Yehova* amalanga aliyense amene iye amamukonda, ndipo amakwapula aliyense amene iye amamuona kuti ndi mwana wake.”+
7 Muyenera kupirira kuti muphunzitsidwe.* Mulungu akuchita nanu zinthu ngati ana ake.+ Ndi mwana wanji amene bambo ake samupatsa chilango?+ 8 Koma ngati simunalandire chilango chimene tonsefe tiyenera kulandira, ndiye kuti ndinu ana a munthu wina, osati ana ake enieni. 9 Bambo athu otibereka ankatilanga ndipo tinkawalemekeza. Ndiye kuli bwanji Atate wa moyo wathu wauzimu? Kodi sitiyenera kuwagonjera koposa pamenepo kuti tikhale ndi moyo?+ 10 Chifukwa bambo athu otiberekawo, anatilanga kwa nthawi yochepa mogwirizana ndi zimene ankaziona kuti nʼzoyenera, koma Mulungu amatilanga kuti zinthu zitiyendere bwino ndiponso kuti tikhale oyera ngati iyeyo.+ 11 Nʼzoona kuti palibe chilango chimene chimakhala chosangalatsa pa nthawi yomwe ukuchilandira, koma chimakhala chowawa. Komabe pambuyo pake, kwa anthu amene aphunzirapo kanthu pa chilangocho, chimabala chipatso chamtendere, chomwe ndi chilungamo.
12 Choncho limbitsani manja ofooka komanso mawondo olobodoka,+ 13 ndipo pitirizani kuwongola njira zimene mapazi anu akuyendamo+ kuti chiwalo chimene chavulala chisaguluke, koma chichiritsidwe. 14 Muziyesetsa kukhala mwamtendere ndi anthu onse,+ komanso kukhala oyera+ chifukwa ngati munthu si woyera, sadzaona Ambuye. 15 Muonetsetse kuti wina asalephere kulandira kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu, kuti pasatuluke muzu wapoizoni nʼkuyambitsa mavuto komanso kuchititsa kuti ambiri aipitsidwe.+ 16 Muonetsetsenso kuti pakati panu pasakhale wachiwerewere* kapena aliyense wosayamikira zinthu zopatulika ngati Esau, amene anapereka udindo wake monga woyamba kubadwa pousinthanitsa ndi chakudya chodya kamodzi kokha.+ 17 Mukudziwa kuti pambuyo pake, pamene ankafuna kulandira madalitso,* anamukanira. Ngakhale kuti anayesetsa ndi mtima wonse kwinaku akulira,+ kuti bambo ake asinthe maganizo, sizinatheke.
18 Inu simunafike paphiri limene mungathe kulikhudza,+ loyaka moto,+ lokhala ndi mtambo wakuda, mdima wandiweyani, lowombedwa ndi mphepo yamkuntho+ 19 komanso limene panamveka kulira kwa lipenga+ ndi mawu a winawake+ ndipo anthu atawamva, anapempha kuti asawauzenso mawu ena.+ 20 Chifukwa anachita mantha kwambiri ndi lamulo lakuti: “Ngakhalenso nyama iliyonse imene ingakhudze phirilo, iponyedwe miyala.”+ 21 Komanso, zimene anaona kumeneko zinali zoopsa kwambiri moti Mose anati: “Ndikuchita mantha ndipo ndikunjenjemera.”+ 22 Koma mwafika kuphiri la Ziyoni+ ndi mzinda wa Mulungu wamoyo, Yerusalemu wakumwamba,+ kumene kuli angelo ambirimbiri,* 23 pamsonkhano wawo waukulu.+ Kumenenso kuli mpingo wa woyamba kubadwayo, mpingo wa iwo amene mayina awo alembedwa kumwamba. Kumeneko kulinso Mulungu, Woweruza wa onse.+ Kulinso olungama amene akukhala ndi moyo mogwirizana ndi mphamvu ya mzimu woyera+ omwe athandizidwa kukhala angwiro.+ 24 Kulinso Yesu, mkhalapakati+ wa pangano latsopano,+ ndiponso magazi amene awazidwa, omwe amalankhula mʼnjira yabwino kwambiri kuposa magazi a Abele.+
25 Samalani kuti musasiye* kumumvera amene akulankhulayo. Chifukwa ngati omwe anakana kumvera amene anapereka chenjezo la Mulungu padziko lapansi sanapulumuke, ndiye kuli bwanji ifeyo? Nafenso sitidzapulumuka tikapanda kumvera amene amalankhula ali kumwamba.+ 26 Pa nthawiyo, mawu ake anagwedeza dziko lapansi,+ koma tsopano walonjeza kuti: “Ndidzagwedezanso kumwamba, osati dziko lapansi lokha.”+ 27 Mawu akuti “ndidzagwedezanso,” akusonyeza kuti zinthu zimene adzazigwedezezo zidzachotsedwa ndipo zinthu zimenezi sizinapangidwe ndi Mulungu. Adzazichotsa kuti zomwe sizikugwedezeka zitsale. 28 Choncho, popeza kuti tidzalandira Ufumu umene sungagwedezeke, tiyeni tikhalebe okhulupirika kuti Mulungu apitirize kutisonyeza kukoma mtima kwakukulu, kuti tizichita utumiki wopatulika mʼnjira yovomerezeka, moopa Mulungu komanso mwaulemu kwambiri. 29 Chifukwa Mulungu wathu ali ngati moto wowononga.+
13 Pitirizani kukonda abale.+ 2 Musaiwale kuchereza alendo,*+ chifukwa pochita zimenezi, ena anachereza angelo mosadziwa.+ 3 Muzikumbukira amene ali mʼndende+ ngati kuti mwamangidwa nawo limodzi.+ Muzikumbukiranso amene akuzunzidwa, popeza inunso ndinu anthu.* 4 Ukwati ukhale wolemekezeka kwa onse, ndipo pogona pa anthu okwatirana pakhale posadetsedwa,+ chifukwa Mulungu adzaweruza achiwerewere* ndiponso achigololo.+ 5 Musamakonde ndalama,+ koma muzikhutira ndi zimene muli nazo pa nthawiyo.+ Chifukwa Mulungu anati: “Sindidzakusiyani kapena kukutayani ngakhale pangʼono.”+ 6 Tikhale olimba mtima ndithu ndipo tinene kuti: “Yehova* ndi amene amandithandiza. Sindidzaopa. Munthu angandichite chiyani?”+
7 Muzikumbukira amene akukutsogolerani.+ Amenewa anakuphunzitsani mawu a Mulungu. Ndipo pamene mukuganizira zotsatira zabwino za khalidwe lawo, tsanzirani chikhulupiriro chawo.+
8 Yesu Khristu sanasinthe kuyambira dzulo mpaka lero ndipo sadzasintha mpaka kalekale.
9 Musasocheretsedwe ndi ziphunzitso zosiyanasiyana zachilendo. Kukoma mtima kwa Mulungu nʼkumene kungakuthandizeni kukhala olimba,* osati zakudya. Chifukwa anthu amene amangoganizira za zakudya,* siziwapindulitsa.+
10 Ife tili ndi guwa lansembe limene ochita utumiki wopatulika kuchihema alibe ulamuliro wodya zapaguwapo.+ 11 Chifukwa nyama zimene magazi ake, mkulu wa ansembe amalowa nawo mʼmalo oyera ngati nsembe ya machimo, amakaziwotcha kunja kwa msasa.+ 12 Choncho nayenso Yesu anakavutikira kunja kwa geti la mzinda+ kuti ayeretse anthu ndi magazi ake.+ 13 Tiyeni timutsatire kunja kwa msasako, tikunyozedwa ngati mmene iye ananyozedwera.+ 14 Chifukwa panopa tilibe mzinda wokhazikika, koma tikufunitsitsa mzinda umene ukubwerawo.+ 15 Tiyeni nthawi zonse tizitamanda Mulungu kudzera mwa Yesu.+ Kuchita zimenezi kuli ngati nsembe imene tikupereka kwa Mulungu ndipo timagwiritsa ntchito milomo yathu+ polengeza dzina lake.+ 16 Komanso musaiwale kuchita zabwino ndi kugawira ena zomwe muli nazo,+ chifukwa Mulungu amasangalala ndi nsembe zoterozo.+
17 Muzimvera amene akukutsogolerani+ ndipo muziwagonjera+ chifukwa iwo amayangʼanira miyoyo yanu ndipo adzayankha mlandu.+ Muzichita zimenezi kuti azigwira ntchito yawo mosangalala osati modandaula, chifukwa akatero sizingakuyendereni bwino.
18 Pitirizani kutipempherera, chifukwa tikukhulupirira kuti tili ndi chikumbumtima choyera* ndipo tikufuna kuchita zinthu zonse moona mtima.+ 19 Koma makamaka ndikukulimbikitsani kundipempherera, kuti ndibwerere kumeneko mwamsanga.
20 Tsopano, Mulungu wamtendere amene anaukitsa mʼbusa wamkulu+ wa nkhosa amene ali ndi magazi a pangano losatha, Ambuye wathu Yesu, 21 akupatseni zinthu zonse zofunika kuti muchite chifuniro chake. Ndipo kudzera mwa Yesu Khristu, atithandize kuchita zinthu zomusangalatsa. Mulungu alandire ulemerero mpaka kalekale. Ame.
22 Tsopano abale, ndikukupemphani kuti mumvetsere moleza mtima mawu olimbikitsawa, chifukwa kalata imene ndakulemberaniyi si yaitali. 23 Dziwani kuti mʼbale wathu Timoteyo wamasulidwa ndipo ngati angabwere posachedwapa, ndibwera naye limodzi podzakuonani.
24 Mundiperekere moni kwa anthu onse amene akukutsogolerani ndiponso kwa oyera ena onse. Abale a ku Italy+ kuno akukupatsani moni.
25 Kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu kukhale nanu nonsenu.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mʼchilankhulo choyambirira, “Amapanga angelo ake kukhala mizimu.”
Kapena kuti, “mizimu yochita utumiki wopatulika.”
Onani Zakumapeto A5.
Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “kuponya mbewu pansi.” Mbewuzo zikutanthauza ana a Adamu ndi Hava.
Mʼchilankhulo choyambirira, “malo amene mafupa amalumikizana.”
Kapena kuti, “osochera.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “anali munthu.”
Kapena kuti, “mphamvu zawo za kuzindikira.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mphamvu.”
Kapena kuti, “nʼkumagwira mwamphamvu.”
“Nangula” ndi chinthu chimene amachimangirira kusitima ndipo amachiponya pansi pa nyanja kuti sitima ikaima isatengeke ndi mphepo.
Onani Zakumapeto A5.
Onani Zakumapeto A5.
Onani Zakumapeto A5.
Onani Zakumapeto A5.
Onani Zakumapeto A5.
Onani Zakumapeto A5.
Kapena kuti, “mikate yachionetsero.”
Mawu a Chigiriki amene anawamasulira kuti “chivundikiro” angatanthauzenso nsembe imene munthu amapereka kuti Mulungu amukhululukire.
Mʼchilankhulo choyambirira, “maubatizo osiyanasiyana.”
Kapena kuti, “ngʼombe yaikazi imene sinaberekepo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mzimu wamuyaya.”
Kapena kuti, “mpukutuwo.”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mabaibulo ena amati, “anthu sangachititse.”
Onani Zakumapeto A5.
Mʼchilankhulo choyambirira “yawazidwa,” kutanthauza kuti yawazidwa magazi a Yesu.
Kapena kuti, “tiziderana nkhawa.”
Onani Zakumapeto A5.
Mʼchilankhulo choyambirira, “kukhala ngati chionetsero mʼbwalo la masewera.”
Kapena kuti, “musataye ufulu wanu wa kulankhula.”
Kapena kuti, “makolo athu akale.”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Kapena kuti, “chifukwa anamuchitira umboni polandira.”
Pakati pake panali poti adzabereke “mbadwa” kapena kuti “mbewu.”
Kapena kuti, “wodalirika.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Mbewu.”
Kapena kuti, “lamulo lokhudza.”
Kapena kuti, “okhudza kumuika mʼmanda.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Khristu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ndi mtambo waukulu wa mboni.”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mawu amʼchilankhulo choyambirira amene amasuliridwa kuti “chilango” ali ndi matanthauzo ambiri. Akhoza kutanthauza malangizo, kuphunzitsa, kudzudzula, kulimbikitsa, kulanga kapena uphungu.
Onani Zakumapeto A5.
Onani Zakumapeto A5.
Kapena kuti, “chikhale chilango chanu.”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Kapena kuti, “kulandira madalitso ngati cholowa.”
Kapena kuti, “masauzande masauzande.”
Kapena kuti, “musapeze zifukwa zokanira; musanyalanyaze.”
Kapena kuti, “kukomera mtima anthu osawadziwa.”
Mabaibulo ena amati, “ngati kuti inunso mukuvutika nawo limodzi.”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Onani Zakumapeto A5.
Mʼchilankhulo choyambirira, “kungalimbitse mtima wanu.”
Kutanthauza malamulo okhudza zakudya.
Mʼchilankhulo choyambirira, “chabwino.”