UTHENGA WABWINO WOLEMBEDWA NDI YOHANE
1 Pachiyambi, panali wina amene ankadziwika kuti Mawu,+ ndipo Mawuyo anali ndi Mulungu+ komanso Mawuyo anali mulungu.*+ 2 Ameneyu anali ndi Mulungu kuyambira pachiyambi. 3 Zinthu zonse zinakhalako kudzera mwa iye+ ndipo palibe chinthu ngakhale chimodzi chimene chinakhalapo popanda iyeyo.
4 Moyo unakhalapo kudzera mwa iye ndipo moyowo unali kuwala kounikira anthu.+ 5 Kuwalako kukuunika mumdima+ koma mdimawo sunagonjetse kuwalako.
6 Kunabwera munthu wina amene anatumidwa monga nthumwi ya Mulungu. Dzina lake anali Yohane.+ 7 Munthu ameneyu anabwera ngati mboni, kuti adzachitire umboni za kuwala+ nʼcholinga chakuti anthu osiyanasiyana akhulupirire kudzera mwa iye. 8 Sikuti iyeyu anali kuwalako,+ koma anangobwera kudzachitira umboni za kuwalako.
9 Kuwala kwenikweni kumene kumaunikira anthu osiyanasiyana kunali kutatsala pangʼono kubwera mʼdziko.+ 10 Iye anali mʼdziko+ ndipo dziko linakhalapo kudzera mwa iye,+ koma dzikolo silinamudziwe. 11 Anabwera kudziko lakwawo, koma anthu akwawo enieniwo sanamulandire. 12 Komabe onse amene anamulandira, anawapatsa mphamvu kuti akhale ana a Mulungu,+ chifukwa choti ankakhulupirira dzina lake.+ 13 Iwowa sanabadwe kuchokera mwa anthu kapena chifukwa cha kufuna kwa anthu kapenanso chifukwa cha kufuna kwa munthu, koma anabadwa kuchokera kwa Mulungu.+
14 Choncho Mawu ameneyo anakhala ndi thupi la nyama+ ndipo ankakhala pakati pathu. Ife tinaona ulemerero wake, ulemerero wofanana ndi umene mwana wobadwa yekha+ amalandira kuchokera kwa bambo ake. Mulungu ankamukomera mtima kwambiri* komanso ankaphunzitsa choonadi. 15 (Yohane ankachitira umboni za iye, moti ankachita kufuula kuti: “Uyu ndi amene ndinkanena uja kuti, ‘Amene akubwera mʼmbuyo mwangamu ndi wamkulu kuposa ine, chifukwa anakhalapo ine ndisanabadwe.’”)+ 16 Chifukwa chakuti anali ndi kukoma mtima kwakukulu, nthawi zonse tinkalandira kukoma mtima kwakukulu kosefukira. 17 Popeza Chilamulo chinaperekedwa kudzera mwa Mose,+ kukoma mtima kwakukulu+ komanso choonadi zinakhalako kudzera mwa Yesu Khristu.+ 18 Palibe munthu amene anaonapo Mulungu ndi kale lonse,+ mulungu wobadwa yekha+ amene ali pambali pa Atate*+ ndi amene anafotokoza za Mulungu.+
19 Yohane anapereka umboni pamene Ayuda anatumiza ansembe ndi Alevi kuchokera ku Yerusalemu kukamufunsa kuti: “Kodi ndiwe ndani?”+ 20 Iye anavomera ndipo sanakane. Ananena kuti: “Ine si Khristu.” 21 Iwo anamufunsa kuti: “Nanga ndiwe ndani? Ndiwe Eliya kapena?”+ Iye anayankha kuti: “Ayi.” “Kapena ndiwe Mneneri?”+ Iye anayankha kuti: “Ayi!” 22 Choncho iwo anamufunsa kuti: “Nanga ndiwe ndani? Tiuze kuti tikathe kupereka yankho kwa amene atituma. Mwiniwakewe umati ndiwe ndani?” 23 Iye anati: “Ndine mawu a winawake amene akufuula mʼchipululu kuti, ‘Wongolani njira ya Yehova,’*+ monga mmene mneneri Yesaya ananenera.”+ 24 Anthuwo anatumidwa ndi Afarisi. 25 Choncho anamufunsa kuti: “Nanga nʼchifukwa chiyani umabatiza anthu ngati iweyo si iwe Khristu, Eliya kapena Mneneri?” 26 Yohane anawayankha kuti: “Ine ndimabatiza mʼmadzi. Pakati panu paimirira wina amene inu simukumudziwa. 27 Iye ndi amene akubwera mʼmbuyo mwangamu ndipo ine si woyenera kumasula zingwe za nsapato zake.”+ 28 Zinthu zimenezi zinachitikira ku Betaniya, kutsidya la Yorodano, kumene Yohane ankabatiza anthu.+
29 Tsiku lotsatira anaona Yesu akubwera kwa iye, ndipo anati: “Taonani, Mwanawankhosa+ wa Mulungu amene akuchotsa uchimo+ wa dziko!+ 30 Uyu ndi amene ndinkanena uja kuti: ‘Amene akubwera mʼmbuyo mwangamu ndi wamkulu kuposa ine,* chifukwa anakhalapo ine ndisanabadwe.’+ 31 Inenso sindinkamudziwa, koma chifukwa chimene ndikubatizira anthu mʼmadzi nʼchakuti iyeyu aonekere kwa Isiraeli.”+ 32 Yohane anachitiranso umboni kuti: “Ndinaona mzimu ukutsika ngati nkhunda kuchokera kumwamba ndipo unakhalabe pa iye.+ 33 Inenso sindinkamudziwa, koma Mulungu amene anandituma kudzabatiza mʼmadzi anandiuza kuti: ‘Ukadzaona mzimu ukutsika nʼkukhazikika pamunthu wina,+ ameneyo ndi amene amabatiza ndi mzimu woyera.’+ 34 Ine ndinaonadi zimenezo ndipo ndachitira umboni kuti iyeyu ndi Mwana wa Mulungu.”+
35 Tsiku lotsatira Yohane analinso ataima ndi ophunzira ake awiri, 36 ndipo ataona Yesu akuyenda, ananena kuti: “Onani, Mwanawankhosa+ wa Mulungu!” 37 Ophunzira awiriwo atamumva akunena zimenezi, anatsatira Yesu. 38 Kenako Yesu anacheuka, ndipo atawaona akumutsatira, anawafunsa kuti: “Kodi mukufunafuna chiyani?” Iwo anati: “Rabi, (dzina limeneli akalimasulira limatanthauza, “Mphunzitsi”) kodi mumakhala kuti?” 39 Iye anawauza kuti: “Tiyeni mukaoneko.” Choncho anapita kukaona kumene ankakhala ndipo anakhala naye tsiku limenelo. Apa nʼkuti nthawi ili cha mʼma 4 koloko madzulo.* 40 Andireya,+ mchimwene wake wa Simoni Petulo anali mmodzi wa awiriwo, amene anamva zimene Yohane ananena nʼkutsatira Yesu. 41 Choyamba iyeyu anakumana ndi mchimwene wake Simoni ndipo anamuuza kuti: “Ifetu tapeza Mesiya”+ (dzina limeneli akalimasulira limatanthauza, “Khristu”), 42 ndipo anapita naye kwa Yesu. Yesu atamuyangʼana anati: “Iwe ndiwe Simoni+ mwana wa Yohane, dzina lako likhala Kefa” (limene kumasulira kwake ndi “Petulo”).+
43 Tsiku lotsatira, Yesu anaganiza zoti apite ku Galileya. Ndiyeno anakumana ndi Filipo+ nʼkumuuza kuti: “Ukhale wotsatira wanga.” 44 Filipo anali wochokera ku Betsaida, mzinda umene kunkachokera Andireya ndi Petulo. 45 Kenako Filipo anakumana ndi Natanayeli+ nʼkumuuza kuti: “Ife tapeza Yesu, mwana wa Yosefe,+ wa ku Nazareti. Chilamulo cha Mose komanso zimene aneneri analemba zimanena za iyeyu.” 46 Koma Natanayeli anamufunsa kuti: “Kodi mu Nazareti mungatuluke munthu aliyense wabwino?” Filipo anamuuza kuti: “Tiye ukaone.” 47 Yesu ataona Natanayeli akubwera kumene iye anali, ananena kuti: “Onani Mwisiraeli ndithu, amene mwa iye mulibe chinyengo.”+ 48 Natanayeli anamufunsa kuti: “Mwandidziwa bwanji?” Yesu anamuyankha kuti: “Filipo asanakuitane, ine ndinakuona uli pansi pa mtengo wamkuyu paja.” 49 Natanayeli anamuyankha kuti: “Rabi, ndinu Mwana wa Mulungu, ndinu Mfumu ya Isiraeli.”+ 50 Yesu anamuyankha kuti: “Kodi wakhulupirira chifukwa choti ndakuuza kuti ndinakuona uli pansi pa mtengo wamkuyu? Udzaona zinthu zazikulu kuposa zimenezi.” 51 Kenako anamuuza kuti: “Ndithu ndikukuuzani anthu inu, mudzaona kumwamba kutatseguka, angelo a Mulungu akukwera ndi kutsika kupita kumene kuli Mwana wa munthu.”+
2 Pa tsiku lachitatu, ku Kana wa ku Galileya kunali phwando la ukwati ndipo mayi ake a Yesu analinso komweko. 2 Yesu ndi ophunzira ake anaitanidwanso kuphwando la ukwatilo.
3 Vinyo atatha, mayi ake a Yesu anamuuza kuti: “Vinyo wawathera.” 4 Koma Yesu anauza mayi akewo kuti: “Ndiye ife zikutikhudza bwanji mayi?* Nthawi yanga sinafike.” 5 Mayi akewo anauza amene ankatumikira kuti: “Muchite chilichonse chimene angakuuzeni.” 6 Pamalopo panali mbiya zamiyala zokwana 6, mogwirizana ndi malamulo a Ayuda a kudziyeretsa.+ Mbiya iliyonse inali ya malita pafupifupi 44 mpaka 66.* 7 Choncho Yesu anawauza kuti: “Dzazani mbiyazi ndi madzi.” Iwo anazidzazadi mpaka pakamwa. 8 Ndiyeno anawauza kuti: “Tsopano tunganimo pangʼono mukapereke kwa woyangʼanira phwandoli.” Iwo anakaperekadi. 9 Woyangʼanira phwando uja analawa madzi amene anawasandutsa vinyowo. Popeza kuti sanadziwe kumene wachokera (ngakhale kuti otumikira amene anatunga madziwo ankadziwa), woyangʼanira phwandoyo anaitana mkwati 10 nʼkumuuza kuti: “Munthu aliyense amatulutsa vinyo wabwino choyamba ndipo anthu akaledzera, mʼpamene amatulutsa wosakoma kwenikweni. Koma iwe wasunga vinyo wabwino mpaka nthawi ino.” 11 Yesu anachita zimenezi ku Kana wa ku Galileya monga chiyambi cha zizindikiro zake. Iye anaonetsa ulemerero wake+ ndipo ophunzira ake anayamba kumukhulupirira.
12 Zimenezi zitachitika, Yesu, mayi ake, azichimwene ake+ ndi ophunzira ake anapita ku Kaperenao,+ koma sanakhaleko masiku ambiri.
13 Tsopano Pasika+ wa Ayuda anali atayandikira, choncho Yesu ananyamuka nʼkupita ku Yerusalemu. 14 Kumeneko anapeza ogulitsa ngʼombe, nkhosa ndi nkhunda+ komanso osintha ndalama ali mʼkachisi atakhala mʼmipando yawo. 15 Choncho anapanga chikwapu chazingwe nʼkuthamangitsa onse amene anali ndi nkhosa komanso ngʼombe mʼkachisimo. Anakhuthula makobidi a anthu osintha ndalama nʼkugubuduza matebulo awo.+ 16 Ndiyeno anauza ogulitsa nkhundawo kuti: “Chotsani izi muno! Musiyiretu kusandutsa nyumba ya Atate wanga kukhala nyumba ya malonda!”*+ 17 Ophunzira ake anakumbukira zimene Malemba amanena kuti: “Kudzipereka kwanga panyumba yanu kudzakhala ngati moto umene ukuyaka mumtima mwanga.”+
18 Koma Ayudawo ananena kuti: “Utionetsa chizindikiro chotani+ chosonyeza kuti uli ndi ulamuliro wochitira zinthu zimenezi?” 19 Yesu anawayankha kuti: “Gwetsani kachisiyu ndipo ine ndidzamumanga mʼmasiku atatu.”+ 20 Ndiyeno Ayudawo ananena kuti: “Kachisi ameneyu anamangidwa kwa zaka 46, ndiye iwe ukuti udzamumanga mʼmasiku atatu?” 21 Koma iye ankanena za kachisi wa thupi lake.+ 22 Choncho atauka kwa akufa, ophunzira ake anakumbukira kuti ankanena zimenezi+ ndipo anakhulupirira malemba komanso mawu amene Yesu ananena.
23 Ndiyeno ali mu Yerusalemu pachikondwerero cha Pasika, anthu ambiri anamukhulupirira* ataona zizindikiro zimene ankachita. 24 Koma Yesu sanawakhulupirire kwenikweni chifukwa onsewo ankawadziwa, 25 ndipo sankafunika wina woti achite kumuuza za munthu, chifukwa iye ankadziwa zimene zili mumtima mwa munthu.+
3 Panali Mfarisi wina dzina lake Nikodemo,+ wolamulira wa Ayuda. 2 Iyeyu anapita kwa Yesu usiku+ nʼkumuuza kuti: “Rabi,+ tikudziwa kuti inu ndi mphunzitsi wochokera kwa Mulungu, chifukwa palibe munthu amene angathe kuchita zizindikiro+ zimene inu mumachita ngati Mulungu sali naye.”+ 3 Poyankha Yesu anamuuza kuti: “Ndithudi ndikukuuza, munthu sangathe kuona Ufumu wa Mulungu+ ngati sangabadwenso.”*+ 4 Nikodemo anafunsa kuti: “Munthu angabadwe bwanji ali wamkulu kale? Kodi angathe kulowa mʼmimba mwa mayi ake nʼkubadwanso?” 5 Yesu anayankha kuti: “Ndithudi ndikukuuza, munthu sangathe kulowa mu Ufumu wa Mulungu ngati atapanda kubadwa mwa madzi+ ndi mzimu.+ 6 Chimene chabadwa kuchokera mʼthupi nʼchanyama, ndipo chimene chabadwa kuchokera mumzimu nʼchauzimu. 7 Usadabwe chifukwa ndakuuza kuti: Anthu inu muyenera kubadwanso. 8 Mphepo imawombera kumene ikufuna ndipo munthu amamva mkokomo wake, koma sadziwa kumene ikuchokera ndi kumene ikupita. Nʼchimodzimodzi ndi aliyense amene wabadwa kuchokera mumzimu.”+
9 Poyankha Nikodemo anati: “Zimenezi zingatheke bwanji?” 10 Yesu anamufunsa kuti: “Kodi si paja ndiwe mphunzitsi wa Isiraeli, ndiye zikutheka bwanji kuti usadziwe zinthu zimenezi? 11 Ndithudi ndikukuuza, zimene ife tikudziwa timazilankhula, ndipo zimene taona timazichitira umboni. Koma inu simulandira umboni umene timapereka. 12 Ngati ndakuuzani zinthu zapadziko lapansi koma inu simukukhulupirirabe, ndiye mungakhulupirire bwanji nditakuuzani zinthu zakumwamba? 13 Ndipotu palibe munthu amene anakwera kumwamba+ koma Mwana wa munthu yekha, amene anatsika kuchokera kumwambako.+ 14 Mofanana ndi Mose amene anakweza njoka mʼmwamba mʼchipululu,+ Mwana wa munthunso akuyenera kukwezedwa mʼmwamba+ 15 kuti aliyense womukhulupirira akhale ndi moyo wosatha.+
16 Chifukwa Mulungu anakonda kwambiri dziko moti anapereka Mwana wake wobadwa yekha,+ kuti aliyense womukhulupirira asawonongedwe koma akhale ndi moyo wosatha.+ 17 Mulungu sanatumize Mwana wake mʼdziko kuti mwanayo adzaweruze dziko, koma kuti dzikolo lipulumutsidwe kudzera mwa iye.+ 18 Aliyense amene amamukhulupirira sayenera kuweruzidwa.+ Aliyense amene samukhulupirira waweruzidwa kale, chifukwa sanakhulupirire mʼdzina la Mwana wobadwa yekha wa Mulungu.+ 19 Kuwala kwafika mʼdziko+ koma mʼmalo mokonda kuwala anthu akukonda mdima popeza ntchito zawo nʼzoipa, nʼchifukwa chake adzaweruzidwe. 20 Amene amachita zinthu zoipa amadana ndi kuwala ndipo safika pamene pali kuwala, kuti ntchito zake zisaonekere.* 21 Koma aliyense amene amachita zinthu zabwino amabwera pamene pali kuwala,+ kuti ntchito zake zionekere kuti anazichita mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu.”
22 Zimenezi zitatha Yesu ndi ophunzira ake anapita mʼdera lakumudzi la ku Yudeya. Iye anakhala nawo kumeneko kwa kanthawi ndipo ankabatiza anthu.+ 23 Koma Yohane nayenso ankabatiza anthu ku Ainoni pafupi ndi Salimu, chifukwa kumeneko kunali madzi ambiri+ ndipo anthu ankapita kukabatizidwa.+ 24 Pa nthawiyi nʼkuti Yohane asanamutsekere mʼndende.+
25 Tsopano ophunzira a Yohane anayamba kukangana ndi Myuda wina pa nkhani yokhudza kukhala oyera pamaso pa Mulungu. 26 Pambuyo pake anapita kwa Yohane nʼkumuuza kuti: “Rabi, munthu amene munali naye kutsidya kwa Yorodano uja, amene munkamuchitira umboni uja,+ iyenso akubatiza ndipo anthu onse akupita kwa iye.” 27 Poyankha Yohane anati: “Munthu sangalandire kanthu kalikonse pokhapokha atapatsidwa kuchokera kumwamba. 28 Inunso ndinu mboni pa zimene ndinanena kuti, ‘Ine si Khristu,+ koma ndinatumizidwa monga kalambulabwalo wake.’+ 29 Munthu amene ali ndi mkwatibwi ndi mkwati.+ Koma mnzake wa mkwati, akaimirira ndi kumvetsera zimene akunena, amasangalala kwambiri chifukwa cha mawu a mkwatiyo. Choncho ine ndikusangalala kwambiri. 30 Iyeyo akuyenera kumawonjezereka, koma ine ndikuyenera kumacheperachepera.”
31 Wochokera kumwamba+ amaposa ena onse. Wochokera padziko lapansi ndi wapadziko lapansi ndipo amalankhula zinthu zapadziko lapansi. Koma wochokera kumwamba ndi woposa ena onse.+ 32 Iye akuchitira umboni zinthu zimene waziona ndi kuzimva,+ koma palibe munthu amene akukhulupirira umboni wake.+ 33 Amene wakhulupirira umboni wakewo watsimikizira* kuti Mulungu amanena zoona.+ 34 Amene anatumidwa ndi Mulungu amalankhula mawu a Mulungu,+ chifukwa Iye akafuna kupereka mzimu sapereka moumira.* 35 Atate amakonda Mwana+ ndipo anapereka zinthu zonse mʼmanja mwake.+ 36 Amene amakhulupirira Mwanayo adzalandira moyo wosatha.+ Wosamvera Mwanayo sadzalandira moyowu,+ koma mkwiyo wa Mulungu udzakhalabe pa iye.+
4 Ambuye atazindikira kuti Afarisi anamva kuti iyeyo* akuphunzitsa anthu ambiri kuti akhale ophunzira ake komanso kuwabatiza+ kuposa Yohane, 2 ngakhale kuti kwenikweni si Yesu amene ankawabatiza koma ophunzira ake, 3 anachoka ku Yudeya nʼkupitanso ku Galileya. 4 Koma anafunika kuti adzere ku Samariya. 5 Choncho anafika mumzinda wa Samariya wotchedwa Sukari, pafupi ndi munda umene Yakobo anapatsa mwana wake Yosefe.+ 6 Ndipotu kumeneko kunali chitsime cha Yakobo.+ Ndiye Yesu atatopa ndi ulendowo, anakhala pansi pachitsimepo.* Nthawi nʼkuti ili cha mʼma 12 koloko masana.*
7 Ndiyeno mayi wina wa mu Samariya anafika kudzatunga madzi. Yesu anapempha mayiyo kuti: “Mundigawireko madzi akumwa mayi.” 8 (Ophunzira ake anali atalowa mumzinda kukagula chakudya.) 9 Ndiye mayi wa Chisamariyayo anafunsa Yesu kuti: “Popeza inu ndinu Myuda, bwanji mukupempha madzi akumwa kwa ine, mayi wa Chisamariya?” (Chifukwa Ayuda ndi Asamariya sagwirizana.)+ 10 Poyankha Yesu anauza mayiyo kuti: “Mukanadziwa za mphatso yaulere ya Mulungu+ komanso amene akukuuzani kuti, ‘Mundigawireko madzi akumwa,’ mukanamupempha iyeyo ndipo akanakupatsani madzi amoyo.”+ 11 Mayiyo anamuuza kuti: “Bambo, mulibe nʼchotungira chomwe ndipo chitsimechi nʼchozama. Ndiye madzi amoyowo mwawatenga kuti? 12 Kodi ndinu wamkulu kuposa kholo lathu Yakobo, amene anatipatsa chitsimechi, chimenenso iyeyo, ana ake ndi ngʼombe zake ankamwa?” 13 Poyankha, Yesu anamuuza kuti: “Aliyense amene wamwa madzi awa adzamvanso ludzu. 14 Koma amene adzamwe madzi amene ine ndidzamupatse sadzamvanso ludzu ngakhale pangʼono.+ Madzi amene ndidzamupatsewo adzasanduka kasupe wa madzi amene akutuluka mwa iye nʼkumupatsa moyo wosatha.”+ 15 Mayiyo anauza Yesu kuti: “Bambo, ndipatseni madzi amenewo, kuti ndisadzamvenso ludzu komanso kuti ndisamabwerenso kuno kudzatunga madzi.”
16 Iye anauza mayiyo kuti: “Pitani, mukaitane mwamuna wanu abwere kuno.” 17 Mayiyo anayankha kuti: “Ndilibe mwamuna.” Yesu anamuuza kuti: “Mwanena zoona poyankha kuti, ‘Ndilibe mwamuna.’ 18 Chifukwa mwakwatiwapo ndi amuna 5, ndipo mwamuna amene muli naye panopa si mwamuna wanu. Apa mwanenadi zoona.” 19 Mayiyo anamuuza kuti: “Bambo, ndazindikira kuti ndinu mneneri.+ 20 Makolo athu ankalambira mʼphiri ili, koma anthu inu mumanena kuti malo amene anthu akuyenera kulambirirako Mulungu ali ku Yerusalemu.”+ 21 Yesu anauza mayiyo kuti: “Ndithu ndikukuuzani mayi, nthawi idzafika pamene inu simudzalambira Atate mʼphiri ili kapena ku Yerusalemu. 22 Inu mumalambira chimene simuchidziwa.+ Ife timalambira chimene tikuchidziwa, chifukwa chipulumutso chikuyambira kwa Ayuda.+ 23 Komabe nthawi idzafika, ndipo ndi yomwe ino, pamene olambira oona adzalambira Atate motsogoleredwa ndi mzimu ndi choonadi, chifukwa Atate akufuna kuti anthu ngati amenewo azimulambira.+ 24 Mulungu ndi Mzimu,+ ndipo amene akumulambira akuyenera kumulambira motsogoleredwa ndi mzimu komanso choonadi.”+ 25 Mayiyo ananena kuti: “Ndikudziwa kuti Mesiya akubwera, amene amadziwikanso kuti Khristu. Ameneyo akadzabwera, adzatifotokozera zonse poyera.” 26 Yesu anamuuza kuti: “Munthu ameneyo ndi ineyo, amene ndikulankhula nanu.”+
27 Pa nthawiyo ophunzira ake anafika, ndipo anadabwa chifukwa ankalankhula ndi munthu wamkazi. Komabe palibe amene ananena kuti: “Mukufuna chiyani kwa iye?” kapena kuti, “Nʼchifukwa chiyani mukulankhula ndi mayiyu?” 28 Choncho mayi uja anasiya mtsuko wake wa madzi nʼkukalowa mumzinda ndipo anauza anthu kuti: 29 “Tiyeni mukaone munthu amene wandiuza zonse zimene ndakhala ndikuchita. Kodi ameneyu sangakhale Khristu uja?” 30 Iwo anatuluka mumzindawo nʼkupita kumene kunali Yesu.
31 Apa nʼkuti ophunzira ake akumupempha kuti: “Rabi,+ idyani.” 32 Koma iye anawauza kuti: “Ndili ndi chakudya chimene inu simukuchidziwa.” 33 Ndiyeno ophunzirawo anayamba kufunsana kuti: “Pali amene wamubweretsera chakudya ngati?” 34 Yesu anawauza kuti: “Chakudya changa ndi kuchita zofuna za amene anandituma+ ndi kumaliza ntchito yake.+ 35 Kodi inu simunena kuti kwatsala miyezi 4 kuti tiyambe kukolola? Koma ndikukuuzani kuti: Kwezani maso anu muone mʼmindamo. Muona kuti mwayera kale ndipo mʼmofunika kukolola.+ Moti pano 36 wokolola akulandira malipiro ndipo akusonkhanitsa zipatso ku moyo wosatha, kuti wofesa mbewu ndi wokolola asangalalire limodzi.+ 37 Nʼchifukwa chake mawu akuti: Wina ndi wofesa ndipo wina ndi wokolola, ndi owona. 38 Ine ndakutumizani kukakolola zimene simunakhetsere thukuta. Ena anagwira ntchito mwakhama ndipo inu mukupindula ndi ntchito imene iwo anagwira.”
39 Asamariya ambiri ochokera mumzindawo anakhulupirira mwa iye chifukwa cha mawu a mayi uja. Mayiyo anachitira umboni kuti: “Iyeyu wandiuza zinthu zonse zimene ndakhala ndikuchita.”+ 40 Choncho Asamariyawo atafika kwa iye, anamupempha kuti akhalebe nawo ndipo anakhala kumeneko masiku awiri. 41 Zotsatira zake, anthu ochuluka anakhulupirira chifukwa cha zimene iye ananena, 42 ndipo anauza mayi uja kuti: “Sikuti tikukhulupirira chifukwa cha mawu ako okha aja ayi, chifukwa tadzimvera tokha ndipo tikudziwa kuti munthu uyu ndi mpulumutsidi wa dziko.”+
43 Masiku awiriwo atatha, iye anachoka kumeneko nʼkupita ku Galileya. 44 Yesu mwiniwakeyo anachitira umboni kuti mneneri salemekezedwa kwawo.+ 45 Choncho atafika ku Galileya, anthu a ku Galileyako anamulandira chifukwa anali ataona zonse zimene anachita pachikondwerero ku Yerusalemu,+ popeza nawonso anapita kuchikondwereroko.+
46 Kenako anafikanso ku Kana wa ku Galileya, kumene anasandutsa madzi kukhala vinyo kuja.+ Tsopano kumeneku kunali munthu wina amene ankatumikira mfumu, amene mwana wake wamwamuna ankadwala ku Kaperenao. 47 Munthuyu atamva kuti Yesu wafika ku Galileya kuchokera ku Yudeya, anapita kwa iye kukamupempha kuti apite ku Kaperenao nʼkukachiritsa mwana wakeyo, chifukwa anali atatsala pangʼono kumwalira. 48 Koma Yesu anamuuza kuti: “Anthu inu simungakhulupirire ngakhale pangʼono pokhapokha mutaona zizindikiro ndi zodabwitsa.”+ 49 Mtumiki wa mfumu uja anamuuza kuti: “Ambuye, tiyeni mwana wanga asanafe.” 50 Yesu anamuuza kuti: “Pita, mwana wako ali moyo.”+ Munthuyo anakhulupirira mawu amene Yesu anamuuzawo ndipo anapitadi. 51 Koma ali mʼnjira, akapolo ake anamuchingamira kudzamuuza kuti mnyamata wake ali moyo.* 52 Choncho iye anawafunsa ola limene anachira ndipo iwo anamuyankha kuti: “Malungo* ake atha dzulo cha mʼma 1 koloko masana.”* 53 Atatero bamboyo anadziwa kuti linali ola lomwelo pamene Yesu anamuuza kuti: “Mwana wako ali moyo.”+ Choncho iye ndi banja lake lonse anakhulupirira. 54 Chimenechi chinali chizindikiro chachiwiri+ chimene Yesu anachita atachoka ku Yudeya nʼkupita ku Galileya.
5 Pambuyo pa zimenezi, kunali chikondwerero+ cha Ayuda ndipo Yesu ananyamuka kupita ku Yerusalemu. 2 Ku Yerusalemu pa Geti la Nkhosa+ pali damu limene mʼChiheberi limatchedwa Betizata. Mʼmbali mwa damulo muli makonde 5 amene ali ndi zipilala. 3 Mmenemu munkagona anthu ambiri odwala, osaona, olumala komanso akufa ziwalo. 4*—— 5 Panalinso mwamuna wina amene anakhala akudwala kwa zaka 38. 6 Ataona munthu ameneyu ali chigonere, komanso atadziwa kuti wakhala akudwala nthawi yaitali, Yesu anamufunsa kuti: “Kodi ukufuna kuchira?”+ 7 Munthu wodwalayo anamuyankha kuti: “Bambo, palibe munthu woti andiviike mʼdamuli madzi akawinduka, ndipo ndikati ndikalowemo wina akumandipitirira nʼkukalowa.” 8 Yesu anamuuza kuti: “Nyamuka, nyamula machira akowa nʼkuyamba kuyenda.”+ 9 Nthawi yomweyo munthu uja anachira ndipo ananyamula machira akewo nʼkuyamba kuyenda.
Limeneli linali tsiku la Sabata. 10 Choncho Ayuda anayamba kuuza munthu amene anachiritsidwa uja kuti: “Lero ndi Sabata, nʼzosaloleka kuti unyamule machirawa.”+ 11 Iye anawayankha kuti: “Amene wandichiritsayo wandiuza kuti, ‘Nyamula machira akowa nʼkuyamba kuyenda.’” 12 Iwo anamufunsa kuti: “Ndi ndani amene wakuuza kuti, ‘Nyamula machira nʼkuyamba kuyendaʼ?” 13 Koma munthuyo sanadziwe kuti anali ndani, chifukwa Yesu anali atalowa mʼchigulu cha anthu amene anali pamalopo.
14 Kenako Yesu anakumana ndi munthu uja mʼkachisi nʼkumuuza kuti: “Onatu wachira tsopano. Usakachimwenso kuti chinachake choopsa kuposa matenda chisadzakuchitikire.” 15 Munthu uja anachoka nʼkukauza Ayuda aja kuti Yesu ndi amene wamuchiritsa. 16 Ayudawo atamva zimenezi anayamba kuvutitsa Yesu, chifukwa ankachita zinthu zimenezi pa Sabata. 17 Koma iye anawauza kuti: “Atate wanga akugwirabe ntchito mpaka pano, inenso ndikugwirabe ntchito.”+ 18 Pa chifukwa chimenechi Ayudawo anayamba kufunafuna njira yoti amuphere, chifukwa kuwonjezera pa kuphwanya Sabata, ankanenanso kuti Mulungu ndi Atate wake,+ kudziyesa wofanana ndi Mulungu.+
19 Choncho poyankha Yesu anawauza kuti: “Ndithudi ndikukuuzani, Mwana sangachite chilichonse chimene wangoganiza payekha, koma chokhacho chimene waona Atate wake akuchita.+ Chifukwa zilizonse zimene Atatewo amachita, Mwana amachitanso zomwezo mofanana ndi mmene Atatewo amachitira. 20 Atatewo amakonda Mwana wake+ ndipo amamuonetsa zonse zimene iwo amachita. Iwo adzamuonetsa ntchito zazikulu kuposa zimenezi kuti inu mudabwe.+ 21 Mofanana ndi Atate amene amaukitsa akufa nʼkuwapatsa moyo,+ nayenso Mwana amapereka moyo kwa amene wafuna kuti awapatse.+ 22 Atate saweruza munthu aliyense, koma wapereka udindo wonse woweruza kwa Mwana,+ 23 kuti onse alemekeze Mwana ngati mmene amalemekezera Atate. Aliyense amene salemekeza Mwana salemekezanso Atate amene anamutuma.+ 24 Ndithudi ndikukuuzani, aliyense amene wamva mawu anga nʼkukhulupirira Mulungu amene anandituma, adzapeza moyo wosatha+ ndipo sadzaweruzidwa koma wachoka ku imfa nʼkuwolokera ku moyo.+
25 Ndithudi ndikukuuzani, nthawi ikubwera ndipo ndi inoyi, pamene akufa adzamva mawu a Mwana wa Mulungu ndipo amene akumvera adzakhala ndi moyo. 26 Mofanana ndi Atate amene ali ndi mphamvu zopereka moyo,*+ alolanso Mwana kuti akhale ndi mphamvu zopereka moyo.+ 27 Amupatsanso mphamvu zoweruza,+ chifukwa iye ndi Mwana wa munthu.+ 28 Musadabwe nazo zimenezi, chifukwa nthawi ikubwera imene onse amene ali mʼmanda achikumbutso adzamva mawu ake+ 29 ndipo adzatuluka. Amene ankachita zabwino adzauka kuti alandire moyo ndipo amene ankachita zoipa adzauka kuti aweruzidwe.+ 30 Ine sindingachite chilichonse chimene ndangoganiza pandekha. Ndimaweruza mogwirizana ndi zimene ndamva, ndipo chiweruzo changa nʼcholungama,+ chifukwa sindichita zofuna zanga, koma zofuna za amene anandituma.+
31 Ngati ndikudzichitira umboni ndekha ndiye kuti umboni wangawo si woona.+ 32 Alipo wina amene akuchitira umboni za ine ndipo ndikudziwa kuti umboni umene akundichitirawo ndi woona.+ 33 Inu munatumiza anthu kwa Yohane, ndipo iye wachitira umboni choonadi.+ 34 Komatu ine sindivomereza umboni wochokera kwa munthu, koma ndikunena zimenezi kuti inu mupulumuke. 35 Munthu ameneyu anali nyale yoyaka komanso yowala, ndipo kwa kanthawi kochepa inu munali ofunitsitsa kusangalala kwambiri chifukwa cha kuwala kwakeko.+ 36 Koma ine ndili ndi umboni woposa wa Yohane, chifukwa ntchito zimene Atate wanga anandipatsa kuti ndizikwaniritse, ntchito zimene ndikuchitazi, zikuchitira umboni kuti Atate ananditumadi.+ 37 Komanso Atate amene anandituma andichitira umboni.+ Inu simunamvepo mawu ake nthawi ina iliyonse kapena kuona thupi lake.+ 38 Mawu akenso sanakhazikike mwa inu, chifukwa simunakhulupirire amene Atatewo anamutumiza.
39 Inu mumafufuza mʼMalemba+ chifukwa mumaganiza kuti mudzapeza moyo wosatha kudzera mʼMalembawo ndipo Malemba omwewo ndi amenenso amachitira umboni za ine.+ 40 Koma simukufuna kubwera kwa ine+ kuti mudzapeze moyo. 41 Sindikufuna ulemerero wochokera kwa anthu, 42 koma ndikudziwa bwino ndithu kuti mʼmitima yanu mulibe chikondi cha Mulungu. 43 Ine ndabwera mʼdzina la Atate wanga koma simunandilandire. Koma wina akanabwera mʼdzina lake, mukanamulandira ameneyo. 44 Mungakhulupirire bwanji pamene mukulandira ulemerero kuchokera kwa anthu anzanu, koma osayesetsa kuti mupeze ulemerero wochokera kwa Mulungu yekhayo?+ 45 Musaganize kuti ine ndikakunenezani kwa Atate. Alipo amene amakunenezani, yemwe ndi Mose+ amene mumamudalira. 46 Ndipotu ngati mukanakhulupirira Mose, mukanakhulupiriranso ine, chifukwa iyeyo analemba za ine.+ 47 Koma ngati simukhulupirira zimene analembazo, ndiye mungakhulupirire bwanji mawu anga?”
6 Pambuyo pa zimenezi, Yesu anawolokera kutsidya lina la nyanja ya Galileya,* kapena kuti nyanja ya Tiberiyo.+ 2 Ndipo gulu lalikulu la anthu linkamutsatira+ chifukwa linkaona zizindikiro zimene iye ankachita pochiritsa anthu odwala.+ 3 Choncho Yesu anakwera mʼphiri ndipo anakhala pansi pamodzi ndi ophunzira ake. 4 Tsopano chikondwerero cha Ayuda cha Pasika+ chinali chitayandikira. 5 Yesu atakweza maso ake nʼkuona gulu lalikulu la anthu likubwera kwa iye, anafunsa Filipo kuti: “Kodi mitanda ya mkate yodyetsa anthu onsewa tingakaigule kuti?”+ 6 Komatu iye ananena zimenezi pongofuna kumuyesa chifukwa ankadziwa kale zimene akufuna kuchita. 7 Filipo anamuyankha kuti: “Mitanda ya mkate ya ndalama zokwana madinari 200* singawakwanire ngakhale titati aliyense angolandirako pangʼono.” 8 Mmodzi wa ophunzira ake, Andireya mchimwene wake wa Simoni Petulo, anati: 9 “Pali kamnyamata pano kamene kali ndi mitanda 5 ya mkate wa balere ndi tinsomba tiwiri. Koma nanga zimenezi zingakwanire chigulu cha anthu chonsechi?”+
10 Yesu ananena kuti: “Auzeni anthuwa kuti akhale pansi.” Pamalopo panali udzu wambiri. Choncho amuna pafupifupi 5,000 anakhaladi pansi.+ 11 Ndiyeno Yesu anatenga mitanda ya mkate ija. Atayamika, anaigawa kwa anthu onse amene anakhala pansi aja. Anachitanso chimodzimodzi ndi tinsomba tija ndipo anthuwo anadya mmene aliyense anafunira. 12 Anthu onsewo atakhuta, iye anauza ophunzira ake kuti: “Sonkhanitsani zotsala zonse, kuti pasawonongeke chilichonse.” 13 Choncho anatolera zonse, ndipo zinadzaza madengu 12 kuchokera pa mitanda ya mkate wa balere 5 ija, imene onse anadya mpaka kuilephera.
14 Anthuwo ataona chizindikiro chimene anachitacho, anayamba kunena kuti: “Mosakayika uyu ndi mneneri uja amene anati adzabwera padziko.”+ 15 Kenako Yesu atadziwa kuti anthu akufuna kubwera kudzamugwira kuti amuveke ufumu, anachoka+ nʼkupitanso kuphiri yekhayekha.+
16 Chakumadzulo ndithu, ophunzira ake anapita kunyanja.+ 17 Iwo anakwera ngalawa nʼkuyamba kuwoloka nyanja kulowera ku Kaperenao. Pa nthawiyi nʼkuti mdima utagwa ndipo Yesu anali asanabwerebe kwa iwo.+ 18 Komanso nyanja inayamba kuchita mafunde chifukwa kunkawomba mphepo yamphamvu.+ 19 Koma atapalasa makilomita pafupifupi 5 kapena 6,* anaona Yesu akuyenda panyanja kuyandikira ngalawayo ndipo iwo anachita mantha. 20 Koma Yesu anawauza kuti: “Ndine, musachite mantha!”+ 21 Kenako anamulola kuti akwere mʼngalawa yawo, ndipo nthawi yomweyo ngalawa ija inakafika kumtunda kumene ankapita.+
22 Tsiku lotsatira, anthu amene anali kutsidya lina la nyanjayo anaona kuti palibe ngalawa iliyonse. Pamalopo panali ngalawa imodzi yaingʼono, koma Yesu sanakwere ngalawayo limodzi ndi ophunzira ake chifukwa ophunzira akewo anachoka paokha. 23 Koma ngalawa zochokera ku Tiberiyo zinafika pafupi ndi pamalo amene anthuwo anadyera mkate uja Ambuye atayamika. 24 Choncho gulu la anthulo litaona kuti Yesu komanso ophunzira ake kulibe, linakwera ngalawa zawo nʼkupita ku Kaperenao kukafunafuna Yesu.
25 Atamupeza kutsidya kwa nyanjayo anamufunsa kuti: “Rabi,+ mwafika nthawi yanji kuno?” 26 Yesu anawayankha kuti: “Ndithu ndikukuuzani, sikuti mukundifunafuna chifukwa choti munaona zizindikiro ayi, koma chifukwa choti munadya mikate nʼkukhuta.+ 27 Musamagwire ntchito kuti mungopeza chakudya chimene chimawonongeka, koma kuti mupeze chakudya chokhalitsa, chimene chimabweretsa moyo wosatha.+ Mwana wa munthu adzakupatsani chakudya chimenechi chifukwa Atate, Mulungu yekhayo, waika chidindo chake pa iye chomuvomereza.”+
28 Choncho anthuwo anamufunsa kuti: “Kodi titani kuti tizichita zimene Mulungu amafuna?” 29 Yesu anawayankha kuti: “Zimene Mulungu akufuna kuti muzichita ndi zakuti muzisonyeza chikhulupiriro mwa amene anamutuma.”+ 30 Ndiyeno iwo anamufunsa kuti: “Ndiye inuyo muchita chizindikiro chotani+ kuti ife tichione nʼkukukhulupirirani? Muchita ntchito yotani? 31 Makolo athu anadya mana mʼchipululu,+ monga mmene Malemba amanenera kuti: ‘Anawapatsa chakudya chochokera kumwamba kuti adye.’”+ 32 Kenako Yesu anati: “Ndithudi ndikukuuzani, Mose sanakupatseni chakudya chochokera kumwamba, koma Atate wanga amakupatsani chakudya chenicheni chochokera kumwamba. 33 Chifukwa chakudya chimene Mulungu wapereka ndi iye amene wabwera kuchokera kumwamba nʼkupereka moyo kudziko.” 34 Choncho iwo anamuuza kuti: “Ambuye, muzitipatsa chakudya chimenechi nthawi zonse.”
35 Ndiyeno Yesu anawauza kuti: “Ine ndine chakudya chopatsa moyo.* Aliyense wobwera kwa ine sadzamva njala ngakhale pangʼono, ndipo wokhulupirira mwa ine sadzamva ludzu.+ 36 Koma paja ndakuuzani kuti, ngakhale mwandiona, simukukhulupirirabe.+ 37 Aliyense amene Atate adzandipatse adzabwera kwa ine, ndipo amene wabwera kwa ine sindidzamuthamangitsa.+ 38 Chifukwa ndinabwera kuchokera kumwamba+ kudzachita zofuna za amene anandituma, osati zofuna zanga.+ 39 Chifuniro cha amene anandituma ine nʼchakuti, ndisataye aliyense mwa onse amene iye wandipatsa, koma kuti ndidzawaukitse+ pa tsiku lomaliza. 40 Zimene Atate wanga akufuna ndi zoti aliyense wovomereza Mwana komanso kumukhulupirira akhale ndi moyo wosatha,+ ndipo ine ndidzamuukitsa+ pa tsiku lomaliza.”
41 Atatero, Ayudawo anayamba kungʼungʼudza za iye chifukwa ananena kuti: “Ine ndine chakudya chochokera kumwamba.”+ 42 Iwo anayamba kunena kuti: “Kodi uyu si Yesu mwana wa Yosefe, amene bambo ake ndi mayi ake tikuwadziwa?+ Nanga bwanji pano akunena kuti, ‘Ndinachokera kumwambaʼ?” 43 Poyankha Yesu anati: “Siyani kungʼungʼudza inu. 44 Palibe munthu amene angabwere kwa ine pokhapokha Atate amene anandituma atamukoka+ ndipo ine ndidzamuukitsa pa tsiku lomaliza.+ 45 Zinalembedwa mʼMabuku a Aneneri kuti: ‘Onse adzaphunzitsidwa ndi Yehova.’*+ Aliyense amene wamva kwa Atate ndipo waphunzira amabwera kwa ine. 46 Palibe munthu amene anaonapo Atate,+ kupatulapo yekhayo amene anachokera kwa Mulungu, ameneyu anaona Atate.+ 47 Ndithudi ndikukuuzani, aliyense wokhulupirira adzapeza moyo wosatha.+
48 Ine ndine chakudya chopatsa moyo.+ 49 Makolo anu anadya mana mʼchipululu koma anamwalirabe.+ 50 Ichi ndi chakudya chochokera kumwamba, choti aliyense adyeko kuti asamwalire. 51 Ine ndine chakudya chamoyo chochokera kumwamba. Ngati wina atadya chakudya chimenechi adzakhala ndi moyo wosatha. Ndipotu chakudya chimene ndidzapereke kuti dzikoli lipeze moyo, ndi mnofu wangawu.”+
52 Kenako Ayudawo anayamba kutsutsana okhaokha kuti: “Kodi munthu ameneyu angathe bwanji kutipatsa mnofu wake kuti tidye?” 53 Choncho Yesu anawauza kuti: “Ndithudi ndikukuuzani, Mukapanda kudya mnofu wa Mwana wa munthu ndi kumwa magazi ake, simudzapeza moyo.*+ 54 Aliyense amene amadya mnofu wanga ndi kumwa magazi anga adzapeza moyo wosatha, ndipo ndidzamuukitsa+ pa tsiku lomaliza. 55 Chifukwa mnofu wanga ndi chakudya chenicheni ndipo magazi anga ndi chakumwa chenicheni. 56 Aliyense amene amadya mnofu wanga ndi kumwa magazi anga, iyeyo ndi ine timakhala ogwirizana.+ 57 Atate wamoyo anandituma ine ndipo ine ndili ndi moyo chifukwa cha Atate. Mofanana ndi zimenezi, amene akudya mnofu wanga adzakhala ndi moyo chifukwa cha ine.+ 58 Chimenechi ndi chakudya chimene chinachokera kumwamba. Nʼchosiyana ndi chakudya chimene makolo anu anadya koma nʼkumwalirabe. Aliyense wakudya chakudya chimenechi adzakhala ndi moyo wosatha.”+ 59 Ananena zinthu zimenezi pamene ankaphunzitsa mʼsunagoge* ku Kaperenao.
60 Atamva zimenezi, ambiri mwa ophunzira ake anati: “Mawu amenewa ndi ozunguza. Ndi ndani angamvetsere zimenezi?” 61 Koma Yesu atadziwa kuti ophunzira ake akungʼungʼudza chifukwa cha zimene ananenazo, anawafunsa kuti: “Kodi mawuwa mwakhumudwa nawo? 62 Ndiye zidzakhala bwanji mukadzaona Mwana wa munthu akukwera kupita kumene anali poyamba?+ 63 Mzimu ndi umene umapatsa moyo+ koma mnofu ulibe ntchito iliyonse. Mawu amene ndakuuzaniwa ndi mzimu ndiponso ndi moyo.+ 64 Koma pali ena mwa inu amene sakukhulupirira.” Kuchokera pachiyambi, Yesu ankadziwa amene sankakhulupirira komanso amene adzamupereke.+ 65 Iye anapitiriza kunena kuti: “Nʼchifukwa chake ndinakuuzani kuti, palibe munthu amene angabwere kwa ine pokhapokha Atate atamulola.”+
66 Chifukwa cha zimenezi, ophunzira ake ambiri anamusiya nʼkubwerera ku zinthu zakumbuyo+ ndipo sankayendanso naye. 67 Ndiyeno Yesu anafunsa ophunzira ake 12 aja kuti: “Inunso mukufuna kupita kapena?” 68 Simoni Petulo anayankha kuti: “Ambuye, tingapitenso kwa ndani?+ Inu ndi amene muli ndi mawu othandiza munthu kuti adzapeze moyo wosatha.+ 69 Ife takhulupirira ndipo tadziwa kuti inu ndinu Woyera amene Mulungu anamutumiza.”+ 70 Yesu anawauza kuti: “Ine ndinakusankhani inu 12, si choncho?+ Komatu mmodzi wa inu ndi wonenera anzake zoipa.”*+ 71 Kwenikweni ankanena za Yudasi mwana wa Simoni Isikariyoti, chifukwa ameneyu anali kudzamupereka, ngakhale kuti anali mmodzi wa ophunzira 12 aja.+
7 Zimenezi zitatha, Yesu anapitiriza kugwira ntchito yake* mu Galileya. Iye sanafune kuchita zimenezi mu Yudeya chifukwa Ayuda ankafunitsitsa kumupha.+ 2 Koma Chikondwerero cha Misasa cha Ayuda+ chinali chitayandikira. 3 Ndiye azichimwene ake+ anamuuza kuti: “Mupite ku Yudeya kuti ophunzira anunso akaone zimene mukuchita. 4 Chifukwa palibe munthu amene amachita zinthu mwachinsinsi pamene akufuna kudziwika kwa anthu. Ngati inu mumachita zinthu zimenezi, mudzionetsere poyera kudzikoli.” 5 Azichimwene akewo sankamukhulupirira.+ 6 Yesu anawauza kuti: “Nthawi yanga sinafikebe,+ koma kwa inu, nthawi iliyonse imakhala yoyenera. 7 Dziko lilibe chifukwa choti lizidana nanu, koma limadana ndi ine, chifukwa ndimachitira umboni kuti ntchito zake ndi zoipa.+ 8 Inuyo nyamukani mupite kuchikondwereroko. Ine sindipitako panopa, chifukwa nthawi yanga sinafike.”+ 9 Atawauza zimenezi, iye anatsala ku Galileya.
10 Koma azichimwene akewo atanyamuka kupita kuchikondwereroko, iyenso ananyamuka. Sanapite moonekera koma mwachinsinsi. 11 Ndiyeno Ayuda anayamba kumufunafuna kuchikondwereroko. Iwo ankanena kuti: “Kodi munthu ujayu ali kuti?” 12 Ndipo anthu ankanena zinthu zambirimbiri zokhudza iyeyo mʼgulu lonselo. Ena ankanena kuti: “Amene uja ndi munthu wabwino.” Koma ena ankanena kuti: “Ayi si munthu wabwino amene uja. Iye akusocheretsa anthu ambiri.”+ 13 Koma panalibe amene ankalankhula poyera zokhudza iye chifukwa ankaopa Ayuda.+
14 Chikondwererocho chitafika pakatikati, Yesu analowa mʼkachisi ndipo anayamba kuphunzitsa. 15 Ayudawo anadabwa nʼkufunsa kuti: “Kodi munthu ameneyu Malemba+ amenewa anawadziwa* bwanji, popeza sanapite kusukulu?”*+ 16 Yesu anawayankha kuti: “Zimene ine ndimaphunzitsa si zanga, koma ndi za amene anandituma.+ 17 Ngati munthu akufuna kuchita zimene Mulungu amafuna, adzadziwa ngati zimene ndimaphunzitsa zimachokera kwa Mulungu,+ kapena ngati ndimalankhula zamʼmaganizo mwanga. 18 Wolankhula zamʼmaganizo mwake amadzifunira yekha ulemerero. Koma wofunira ulemerero iye amene anamutuma,+ ameneyu ndi woona ndipo mwa iye mulibe chosalungama. 19 Mose anakupatsani Chilamulo,+ si choncho? Komatu palibe ngakhale mmodzi wa inu amene amamvera Chilamulocho. Nanga nʼchifukwa chiyani mukufuna kundipha?”+ 20 Gulu la anthulo linayankha kuti: “Uli ndi chiwanda iwe. Akufuna kukupha ndi ndani?” 21 Poyankha Yesu anawauza kuti: “Ndangochita chinthu chimodzi chokha ndipo nonsenu mukudabwa. 22 Pa chifukwa chimenechi Mose anakupatsani mdulidwe.+ Sikuti mdulidwewo ndi wochokera kwa Mose ayi, koma ndi wochokera kwa makolo akale,+ ndipo mumachita mdulidwe tsiku la sabata. 23 Ngati munthu amadulidwa tsiku la sabata posafuna kuphwanya Chilamulo cha Mose, kodi mukundipsera mtima kwambiri chifukwa ndinachiritsa munthu tsiku la sabata?+ 24 Siyani kuweruza potengera maonekedwe akunja, koma muziweruza ndi chiweruzo cholungama.”+
25 Ndiyeno anthu ena okhala mu Yerusalemu anayamba kunena kuti: “Kodi munthu akufuna kumupha uja si ameneyu?+ 26 Koma taonani! Si uyu akulankhula poyerayu ndipo sakumuuza chilichonse. Kodi olamulirawa atsimikiza tsopano kuti iyeyu ndi Khristu? 27 Komatu ife tikudziwa kumene munthu ameneyu akuchokera.+ Komano Khristuyo akadzabwera, palibe amene adzadziwe kumene wachokera.” 28 Ndiyeno akuphunzitsa mʼkachisimo Yesu anafuula kuti: “Inu mukundidziwa komanso mukudziwa kumene ndikuchokera. Ine sindinabwere mwa kufuna kwanga,+ koma amene anandituma alipodi ndipo inu simukumudziwa.+ 29 Ine ndikumudziwa,+ chifukwa ndine nthumwi yake. Iyeyo ndi amene anandituma.” 30 Choncho iwo anayamba kufufuza njira yomugwirira,+ koma palibe amene anamugwira chifukwa nthawi yake inali isanafike.+ 31 Komabe anthu ambiri mʼgululo anamukhulupirira+ ndipo ankanena kuti: “Kodi Khristu akadzabwera, adzachita zizindikiro zochuluka kuposa zimene munthu uyu wachita?”
32 Afarisi anamva gulu la anthulo likunongʼonezana zimenezi zokhudza iye ndipo ansembe aakulu komanso Afarisi anatuma alonda kuti akamugwire.* 33 Kenako Yesu ananena kuti: “Ndikhala nanube kanthawi pangʼono ndisanapite kwa iye amene anandituma.+ 34 Mudzandifunafuna koma simudzandipeza, ndipo kumene ndidzapiteko inu simudzatha kukafikako.”+ 35 Choncho Ayudawo anayamba kufunsana kuti: “Kodi munthu ameneyu akufuna kupita kuti, kumene ife sitingathe kumupeza? Kapena akufuna kupita kwa Ayuda amene anamwazikana pakati pa Agiriki nʼkukaphunzitsa Agirikiwo? 36 Kodi akutanthauza chiyani pamene akunena kuti, ‘Mudzandifunafuna koma simudzandipeza, ndipo kumene ine ndidzapite inu simudzatha kukafikakoʼ?”
37 Pa tsiku lomaliza, tsiku lalikulu la chikondwererocho,+ Yesu anaimirira nʼkufuula kuti: “Ngati wina akumva ludzu, abwere kwa ine adzamwe madzi.+ 38 Mogwirizana ndi zimene lemba limanena, aliyense wokhulupirira ine, ‘Mkati mwake mwenimwenimo mudzatuluka mitsinje ya madzi amoyo.’”+ 39 Pamenepa ankanena za mzimu umene onse amene anamukhulupirira anali atatsala pangʼono kulandira. Pa nthawiyi nʼkuti anthu asanalandire mzimu+ chifukwa Yesu anali asanalandire ulemerero wake.+ 40 Ena mʼgululo amene anamva mawu amenewa, anayamba kunena kuti: “Ndithu ameneyu ndi Mneneri.”+ 41 Ena ankanena kuti: “Khristu uja ndi ameneyu.”+ Koma ena ankati: “Kodi Khristu angachokere mu Galileya?+ 42 Kodi si paja lemba limanena kuti Khristu adzachokera mwa ana a Davide+ komanso ku Betelehemu,+ mudzi umene Davide ankakhala?”+ 43 Choncho gulu la anthulo linagawanika pa nkhani yokhudza iye. 44 Ena a iwo ankafuna kumugwira,* koma palibe ngakhale mmodzi amene anamukhudza.
45 Kenako alonda aja anabwerera kwa ansembe aakulu ndi Afarisi ndipo iwo anawafunsa kuti: “Nʼchifukwa chiyani simunabwere naye?” 46 Alondawo anayankha kuti: “Palibe munthu amene analankhulapo ngati iyeyu nʼkale lonse.”+ 47 Ndiyeno Afarisiwo anati: “Kodi inunso mwasocheretsedwa? 48 Palibe ndi mmodzi yemwe mwa olamulira kapena Afarisi amene akumukhulupirira, alipo ngati?+ 49 Koma gulu lonse la anthu osadziwa Chilamulowa ndi lotembereredwa.” 50 Nikodemo, amene mʼmbuyomo anapita kwa Yesu, komanso anali mmodzi wa Afarisi, anawauza kuti: 51 “Chilamulo chathu sichiweruza munthu asanafotokoze maganizo ake choyamba nʼkudziwa zimene akuchita, chimatero ngati?”+ 52 Poyankha iwo anamuuza kuti: “Kodi iwenso ndiwe wochokera ku Galileya eti? Fufuza ndipo supeza pamene pamati mʼGalileya mudzatuluka mneneri.”*
8 12 Kenako Yesu analankhula nawonso kuti: “Ine ndine kuwala kwa dziko.+ Aliyense wonditsatira ine sadzayenda mumdima, koma adzakhala ndi kuwala+ kwa moyo.” 13 Choncho Afarisi anauza Yesu kuti: “Iwe umadzichitira wekha umboni koma umboni wakowo si woona ayi.” 14 Poyankha Yesu anati: “Ngakhale kuti ndimadzichitira ndekha umboni, umboni wanga ndi woona, chifukwa ndikudziwa kumene ndinachokera ndi kumene ndikupita.+ Koma inu simukudziwa kumene ndinachokera komanso kumene ndikupita. 15 Inu mumaweruza potengera mmene munthu akuonekera.*+ Inetu sindiweruza munthu aliyense. 16 Koma ndikati ndiweruze, chiweruzo changa chimakhala cholungama, chifukwa sindiweruza ndekha koma ine limodzi ndi Atate amene anandituma timaweruzira limodzi.+ 17 Ndiponso mʼChilamulo chanu chomwechi analembamo kuti: ‘Umboni wa anthu awiri ndi woona.’+ 18 Ineyo pandekha ndimadzichitira umboni ndipo Atate amene anandituma amandichitiranso umboni.”+ 19 Ndiyeno iwo anamufunsa kuti: “Atate wako ali kuti?” Yesu anayankha kuti: “Inu simukundidziwa komanso simukudziwa Atate wanga.+ Mukanandidziwa ine, mukanadziwanso Atate wanga.”+ 20 Yesu ananena mawu amenewa ali mʼmalo osungira zopereka+ pamene ankaphunzitsa mʼkachisi. Koma palibe amene anamugwira, chifukwa nthawi yake inali isanakwanebe.+
21 Choncho iye anawauzanso kuti: “Ine ndikuchoka ndipo mudzandifunafuna, koma mudzafa mudakali ochimwa.+ Kumene ine ndikupita inu simungathe kupitako.”+ 22 Ndiye Ayudawo anayamba kunena kuti: “Kodi akufuna kudzipha? Nanga nʼchifukwa chiyani akunena kuti, ‘Kumene ine ndikupita inu simungathe kupitako?’” 23 Iye anapitiriza kuwauza kuti: “Inu ndinu ochokera pansi pano koma ine ndine wochokera kumwamba.+ Inu ndinu ochokera mʼdziko lino koma ine si wochokera mʼdziko lino. 24 Nʼchifukwa chake ndakuuzani kuti: Inu mudzafa mudakali ochimwa. Chifukwa ngati simukukhulupirira kuti amene munkamuyembekezera uja ndi ine, mudzafa mudakali ochimwa.” 25 Choncho iwo anayamba kunena kuti: “Kodi ndiwe ndani?” Yesu anayankha kuti: “Ndikudzivutitsiranji kulankhula ndi inu? 26 Ndili ndi zambiri zoti ndinene zokhudza inu nʼkupereka chiweruzo. Ndipotu amene anandituma ine amanena zoona, moti zimene ndinamva kwa iye ndi zimene ndikuzilankhula mʼdzikoli.”+ 27 Iwo sanazindikire kuti ankalankhula nawo zokhudza Atate. 28 Kenako Yesu anati: “Mukadzamukweza Mwana wa munthu,+ pamenepo mudzadziwa kuti amene munkamuyembekezera uja ndi ine+ komanso kuti sindichita chilichonse mongoganiza ndekha.+ Koma zimene ndimalankhula zimakhala zogwirizana ndendende ndi zimene Atate anandiphunzitsa. 29 Ndipo amene ananditumayo ali ndi ine. Iye sanandisiye ndekha chifukwa ndimachita zinthu zimene zimamusangalatsa nthawi zonse.”+ 30 Pamene ankalankhula zimenezi, anthu ambiri anayamba kumukhulupirira.
31 Ndiyeno Yesu anapitiriza kuuza Ayuda amene anamukhulupirirawo kuti: “Mukapitiriza kusunga mawu anga, ndiye kuti ndinudi ophunzira anga. 32 Mudzadziwa choonadi+ ndipo choonadi chidzakumasulani.”+ 33 Iwo anamuyankha kuti: “Ifetu ndife ana a Abulahamu ndipo sitinakhalepo akapolo a munthu. Ndiye iwe ukunena bwanji kuti, ‘Mudzamasulidwaʼ?” 34 Yesu anawayankha kuti: “Ndithudi ndikukuuzani, aliyense amene akuchita tchimo ndi kapolo wa tchimo.+ 35 Komanso kapolo sakhala mʼnyumba ya mbuye wake kwamuyaya koma mwana ndi amene amakhalamo kwamuyaya. 36 Choncho ngati Mwana wakumasulani, mudzakhaladi omasuka. 37 Ndikudziwa kuti ndinu mbadwa za Abulahamu. Koma mukufuna kundipha chifukwa simukuvomereza zimene ndikuphunzitsa. 38 Ine ndimalankhula zimene ndinaziona pamene ndinali ndi Atate wanga,+ koma inu mumachita zimene mwamva kwa atate wanu.” 39 Iwo anamuyankha kuti: “Atate wathu ndi Abulahamu.” Yesu anawauza kuti: “Mukanakhala ana a Abulahamu,+ bwezi mukuchita ntchito za Abulahamu. 40 Koma tsopano mukufuna kundipha, munthu amene ndakuuzani choonadi chimene ndinachimva kwa Mulungu.+ Abulahamu sanachite zimenezi. 41 Inu mukuchita ntchito za atate wanu.” Iwo ananena kuti: “Ife sitinabadwe chifukwa cha chiwerewere,* tili ndi Atate mmodzi, Mulungu.”
42 Yesu anawauza kuti: “Mulungu akanakhala Atate wanu, mukanandikonda,+ chifukwa ine ndinachokera kwa Mulungu ndipo ndili pano. Sindinabwere mwakufuna kwanga koma Iyeyo ndi amene anandituma.+ 43 Nʼchifukwa chiyani simukumvetsa zimene ine ndikunena? Nʼchifukwa chakuti simukufuna kumvetsera mawu anga. 44 Inu ndinu ochokera kwa atate wanu Mdyerekezi, ndipo mukufuna kuchita zimene atate wanu amafuna.+ Iye ndi wopha anthu kuchokera pachiyambi+ ndipo sanapitirize kukhala mʼchoonadi, chifukwa mwa iye mulibe choonadi. Akamanena bodza, amangosonyeza mmene alili, chifukwa iye ndi wabodza komanso tate wake wa bodza.+ 45 Koma popeza ine ndimakuuzani zoona, simundikhulupirira. 46 Ndi ndani wa inu amene angapereke umboni wosonyeza kuti ndachita tchimo? Ngati ndimanena zoona, nʼchifukwa chiyani simundikhulupirira? 47 Wochokera kwa Mulungu amamvetsera mawu a Mulungu.+ Nʼchifukwa chake inu simumvetsera, chifukwa si inu ochokera kwa Mulungu.”+
48 Ayudawo anamuyankha kuti: “Kodi tikunama tikamanena kuti, ‘Ndiwe Msamariya+ ndipo uli ndi chiwandaʼ?”+ 49 Yesu anayankha kuti: “Ine ndilibe chiwanda, koma ndikulemekeza Atate wanga ndipo inu mukundinyoza. 50 Komatu ine sindikudzifunira ndekha ulemerero.+ Mulungu ndi amene akufuna kuti ndilemekezedwe ndipo iye ndi woweruza. 51 Ndithudi ndikukuuzani, ngati munthu akusunga mawu anga, sadzaona imfa ngakhale pangʼono.”+ 52 Ayudawo ananena kuti: “Tsopano tadziwa kuti uli ndi chiwanda. Abulahamu anamwalira, chimodzimodzinso aneneri. Koma iwe ukunena kuti, ‘Ngati munthu akusunga mawu anga sadzalawa imfa ngakhale pangʼono.’ 53 Kodi iweyo ndiwe wamkulu kuposa atate wathu Abulahamu amene anamwalira? Aneneri nawonso anamwalira. Ndiye iweyo ukudziona ngati ndani?” 54 Yesu anayankha kuti: “Ngati ndikudzilemekeza ndekha, ndiye kuti ulemerero wanga ndi wopanda pake. Atate wanga ndi amene amandilemekeza,+ amene inu mukunena kuti ndi Mulungu wanu. 55 Chikhalirecho simukumudziwa,+ koma ine ndikumudziwa.+ Ngati ndinganene kuti sindikumudziwa ndingakhale wabodza ngati inu. Koma ndikumudziwa ndithu ndipo ndikusunga mawu ake. 56 Atate wanu Abulahamu ankasangalala kwambiri chifukwa ankayembekezera kuona tsiku langa, moti analionadi ndipo anasangalala.”+ 57 Kenako Ayudawo anati: “Sunakwanitse nʼkomwe zaka 50, ndiye ukuti unamuona Abulahamu?” 58 Yesu anawauza kuti: “Ndithudi ndikukuuzani, Abulahamu asanakhaleko, ine nʼkuti ndilipo kale.”+ 59 Choncho iwo anatola miyala kuti amugende nayo, koma Yesu anabisala nʼkutuluka mʼkachisimo.
9 Akuyenda anaona munthu amene anabadwa ndi vuto losaona. 2 Ophunzira ake anamufunsa kuti: “Rabi,+ anachimwa ndi ndani kuti munthuyu abadwe ndi vuto losaonali? Ndi iyeyu kapena makolo ake?” 3 Yesu anayankha kuti: “Munthuyu kapena makolo ake, onse sanachimwe. Koma izi zinachitika kuti ntchito za Mulungu zionekere kudzera mwa iye.+ 4 Tiyenera kugwira ntchito za Mulungu amene anandituma kudakali masana.+ Usiku ukubwera pamene munthu sangagwire ntchito. 5 Pamene ine ndili mʼdziko, ndine kuwala kwa dzikoli.”+ 6 Atanena zimenezi, analavulira malovu pansi nʼkukanda matope ndi malovuwo, kenako anapaka matopewo mʼmaso mwa munthuyo.+ 7 Ndiyeno anamuuza kuti: “Pita ukasambe mʼdziwe la Siloamu” (dzina limene kumasulira kwake ndi “Otumizidwa”). Choncho anapita kukasamba ndipo anabwerako akuona.+
8 Ndiyeno anthu oyandikana nawo komanso anthu ena amene mʼmbuyomo ankamuona akupemphapempha anayamba kunena kuti: “Kodi uyu si amene ankakhala pansi nʼkumapemphapempha uja?” 9 Ena ankanena kuti: “Ndi yemweyu.” Enanso ankanena kuti: “Ayi, wangofanana naye.” Koma mwiniwakeyo ankawauza kuti: “Inde, ndi ineyo.” 10 Choncho anamufunsa kuti: “Ndiye maso akowa atseguka bwanji?” 11 Iye anayankha kuti: “Munthu wina dzina lake Yesu anakanda matope nʼkuwapaka mʼmaso mwangamu. Kenako anandiuza kuti, ‘Pita ku Siloamu ukasambe.’+ Ndiye ndinapitadi kukasamba ndipo ndayamba kuona.” 12 Atatero anthuwo anamufunsa kuti: “Ali kuti munthu ameneyo?” Iye ananena kuti: “Sindikudziwa.”
13 Iwo anatenga munthu amene poyamba anali wosaona uja nʼkupita naye kwa Afarisi. 14 Tsiku limene Yesu anakanda matope nʼkutsegula maso a munthuyo+ linali la Sabata.+ 15 Pa nthawi imeneyo Afarisi nawonso anayamba kufunsa munthu uja mmene anayambira kuona. Iye anawafotokozera kuti: “Anapaka matope mʼmaso mwanga, ndiye ndinapita kukasamba, basi kenako ndayamba kuona.” 16 Ndiyeno ena mwa Afarisiwo anayamba kunena kuti: “Munthu ameneyu si wochokera kwa Mulungu, chifukwa sasunga Sabata.”+ Ena ankanena kuti: “Kodi munthu wochimwa angachite bwanji zizindikiro ngati zimenezi?”+ Choncho anthuwo anagawanika.+ 17 Afarisiwo anafunsanso munthu amene anali wosaona uja kuti: “Nanga iwe ukuti bwanji za munthu ameneyu, popeza kuti wakutsegula maso?” Munthuyo anati: “Ndi mneneri.”
18 Komabe Ayudawo sanakhulupirire kuti munthuyu analidi wosaona ndipo wayamba kuona, mpaka anaitanitsa makolo ake a munthuyo. 19 Iwo anafunsa makolowo kuti: “Kodi uyu ndi mwana wanu amene mukuti anabadwa wosaona? Nanga zatheka bwanji kuti ayambe kuona?” 20 Makolo akewo anayankha kuti: “Tikudziwa kuti uyu ndi mwana wathu komanso kuti anabadwa wosaona. 21 Koma sitikudziwa kuti zatheka bwanji kuti ayambe kuona panopa, komanso sitikudziwa amene wamutsegula maso. Mufunseni mwiniwakeyu. Ndi wamkulu ameneyu, afotokoze yekha.” 22 Makolo akewo ananena zimenezi chifukwa ankaopa atsogoleri achipembedzo a Chiyuda.+ Chifukwa iwo anali atagwirizana kale kuti ngati wina angavomereze kuti Yesu ndi Khristu, azimuchotsa musunagoge.+ 23 Nʼchifukwa chake makolo akewo ananena kuti: “Ndi wamkulu ameneyu. Mufunseni mwiniwakeyu.”
24 Choncho iwo anaitananso munthu amene anali wosaona uja kachiwiri nʼkumuuza kuti: “Lemekeza Mulungu, ife tikudziwa kuti munthu ameneyu ndi wochimwa.” 25 Iye anayankha kuti: “Zoti ndi wochimwa, ine sindikudziwa. Chimodzi chokha chimene ine ndikudziwa nʼchakuti, poyamba ndinali wosaona koma tsopano ndikuona.” 26 Ndiyeno iwo anamufunsa kuti: “Anakuchita chiyani? Watsegula bwanji maso ako?” 27 Iye anawayankha kuti: “Ndakuuzani kale koma inu simumamvetsera. Nanga nʼchifukwa chiyani mukufuna kumvanso? Kapena inunso mukufuna kukhala ophunzira ake?” 28 Atanena zimenezi, iwo anamunyoza kuti: “Iweyo ndi amene uli wophunzira wa munthu amene uja, koma ife ndi ophunzira a Mose. 29 Tikudziwa kuti Mulungu analankhula ndi Mose, koma za munthu uyu, sitikudziwa kuti akuchokera kuti.” 30 Munthuyo anawayankha kuti: “Zimenezi nʼzodabwitsa ndithu, simukudziwa kumene wachokera, chikhalirecho wanditsegula maso. 31 Tikudziwa kuti Mulungu samvetsera ochimwa,+ koma ngati munthu amaopa Mulungu ndipo amachita chifuniro chake, munthu ameneyo amamumvetsera.+ 32 Kuyambira kalekale sitinamvepo kuti munthu wina watsegula maso a munthu amene anabadwa wosaona. 33 Munthu ameneyu akanakhala kuti si wochokera kwa Mulungu, sakanatha kuchita chilichonse.”+ 34 Poyankha iwo anamuuza kuti: “Wobadwira mu uchimo wokhawokha iwe. Ndiye kodi ukufuna utiphunzitse?” Zitatero anamuchotsa musunagoge!+
35 Yesu anamva kuti munthu uja amuchotsa musunagoge. Ndipo atakumana naye anamufunsa kuti: “Kodi ukukhulupirira Mwana wa munthu?” 36 Munthuyo anayankha kuti: “Kodi mwana wa munthuyo ndi ndani? Ndiuzeni bambo kuti ndimukhulupirire.” 37 Yesu anamuuza kuti: “Wamuona kale, ndipo ndi amene akulankhula nawe panopa.” 38 Iye ananena kuti: “Ndakukhulupirirani Ambuye.” Ndipo anamugwadira. 39 Ndiyeno Yesu ananena kuti: “Ndinabwera mʼdziko lino kudzapereka chiweruzo chakuti, osaona ayambe kuona+ ndipo amene akuona akhale osaona.”+ 40 Afarisi amene anali naye anamva zimenezi, ndipo anafunsa Yesu kuti: “Kodi ifenso ndife osaona?” 41 Yesu anawauza kuti: “Mukanakhala osaona, simukanakhala ndi tchimo. Koma popeza mukunena kuti ‘Tikuona,’ tchimo lanu silidzakhululukidwa.”+
10 “Ndithudi ndikukuuzani, wolowa mʼkhola la nkhosa mochita kukwera pamalo ena, osati kudzera pakhomo, ameneyo ndi wakuba ndiponso wolanda zinthu za ena.+ 2 Koma amene amalowera pakhomo ndi mʼbusa wa nkhosazo.+ 3 Mlonda wapakhomo amamutsegulira+ ndipo nkhosa zimamvera mawu ake.+ Nkhosa zakezo amazitchula mayina nʼkuzitsogolera kutuluka nazo. 4 Akatulutsa nkhosa zake zonse kunja, amazitsogolera ndipo nkhosazo zimamutsatira, chifukwa zimadziwa mawu ake. 5 Sizidzatsatira mlendo koma zidzamuthawa, chifukwa sizidziwa mawu a alendo.” 6 Yesu ananena fanizoli kwa iwo, koma iwo sanamvetse tanthauzo la zimene ankawauzazo.
7 Choncho Yesu anawauzanso kuti: “Ndithudi ndikukuuzani, ine ndine khomo limene nkhosa zimadutsa.+ 8 Onse amene abwera nʼkumanama kuti ndi abusa enieni, ndi akuba komanso olanda zinthu za ena ndipo nkhosa sizinawamvere. 9 Ine ndine khomo. Aliyense wolowa kudzera mwa ine adzapulumuka ndipo azidzalowa ndi kutuluka kukapeza msipu.+ 10 Wakuba amabwera ndi cholinga chofuna kudzaba, kudzapha ndi kudzawononga.+ Koma ine ndabwera kuti nkhosa zikhale ndi moyo komanso kuti zikhale nawo wochuluka. 11 Ine ndine mʼbusa wabwino.+ Mʼbusa wabwino amapereka moyo wake chifukwa cha nkhosa.+ 12 Munthu waganyu, amene si mʼbusa ndipo nkhosazo si zake, akaona mmbulu ukubwera amasiya nkhosazo nʼkuthawa. Ndiyeno mmbuluwo umazigwira nʼkuzibalalitsa. 13 Amachita zimenezi chifukwa iye ndi waganyu ndipo sasamala za nkhosazo. 14 Ine ndine mʼbusa wabwino. Nkhosa zanga ndimazidziwa ndipo nazonso zimandidziwa,+ 15 ngati mmene zilili kuti Atate amandidziwa ndipo inenso ndimadziwa Atate.+ Choncho ndikupereka moyo wanga chifukwa cha nkhosazo.+
16 Ndili ndi nkhosa zina zimene si zamʼkhola ili.+ Zimenezonso ndiyenera kuzibweretsa ndipo zidzamva mawu anga. Zidzakhala gulu limodzi ndipo mʼbusa wawo adzakhala mmodzi.+ 17 Atate amandikonda+ chifukwa chakuti ndikupereka moyo wanga+ kuti ndikaulandirenso. 18 Palibe munthu amene akuchotsa moyo wanga, koma ndikuupereka mwa kufuna kwanga. Ndili ndi mphamvu zoupereka komanso ndili ndi mphamvu zoulandiranso.+ Atate wanga ndi amene anandilamula kuti ndichite zimenezi.”*
19 Apanso Ayuda anagawanika+ chifukwa cha mawu amenewa. 20 Ambiri a iwo ankanena kuti: “Ameneyu ali ndi chiwanda ndipo ndi wamisala. Nʼchifukwa chiyani mukumumvetsera?” 21 Ena ananena kuti: “Amenewa si mawu a munthu wogwidwa ndi chiwanda ayi. Kodi chiwanda chingatsegule maso a anthu osaona?”
22 Pa nthawiyo mu Yerusalemu munachitika Chikondwerero Chopereka Kachisi kwa Mulungu. Inali nyengo yozizira kwambiri 23 ndipo Yesu ankayenda mʼkachisimo mʼkhonde la zipilala la Solomo.+ 24 Kenako Ayuda anamuzungulira nʼkuyamba kumuuza kuti: “Kodi utivutitsa maganizo mpaka liti? Ngati ndiwedi Khristu, tiuze mosapita mʼmbali.” 25 Yesu anawayankha kuti: “Ndakuuzani kale, koma inu simukukhulupirira. Ntchito zimene ine ndikuchita mʼdzina la Atate wanga, zikundichitira umboni.+ 26 Koma inu simukukhulupirira, chifukwa si inu nkhosa zanga.+ 27 Nkhosa zanga zimamva mawu anga. Ine ndimazidziwa ndipo nkhosazo zimanditsatira.+ 28 Ndidzazipatsa moyo wosatha+ ndipo sizidzawonongeka komanso palibe amene adzazitsomphole mʼdzanja langa.+ 29 Nkhosa zimene Atate wanga andipatsa nʼzofunika kuposa zinthu zina zonse, ndipo palibe amene angazitsomphole mʼdzanja la Atate.+ 30 Ine ndi Atate ndife amodzi.”*+
31 Apanso Ayudawo anatola miyala kuti amugende. 32 Yesu anawauza kuti: “Ndakuonetsani ntchito zambiri zabwino zochokera kwa Atate. Ndiye mukufuna kundigenda chifukwa cha ntchito iti mwa zimenezi?” 33 Ayudawo anamuyankha kuti: “Sitikufuna kukugenda chifukwa cha ntchito yabwino, koma chifukwa chonyoza Mulungu.+ Iwe ndiwe munthu wamba koma ukudziyesa mulungu.” 34 Yesu anawafunsa kuti: “Kodi mʼChilamulo chanu sanalembemo kuti, ‘Ine ndanena kuti: “Inu ndinu milungu”’?*+ 35 Ngati anthu amene anatsutsidwa ndi mawu a Mulungu omwe satha mphamvu, anawatchula kuti ‘milungu,’+ 36 kodi inu mukundiuza ine amene Atate anandiyeretsa nʼkunditumiza mʼdziko kuti, ‘Ukunyoza Mulungu,’ chifukwa ndanena kuti, ‘Ndine Mwana wa Mulunguʼ?+ 37 Ngati sindikuchita ntchito za Atate wanga, musandikhulupirire. 38 Koma ngati ndikuzichita, ngakhale simukundikhulupirira, khulupirirani ntchitozo,+ kuti mudziwe ndi kupitirizabe kudziwa kuti Atate ndi ine ndife ogwirizana.”+ 39 Choncho anayesanso kuti amugwire, koma anawazemba.
40 Iye anawolokanso Yorodano nʼkupita kumene Yohane ankabatizira poyamba+ ndipo anakhala kumeneko. 41 Anthu ambiri anabwera kwa iye nʼkuyamba kunena kuti: “Yohane sanachite chizindikiro chilichonse, koma zonse zimene Yohane ananena zokhudza munthu uyu zinali zoona.”+ 42 Choncho anthu ambiri kumeneko anamukhulupirira.
11 Tsopano panali munthu wina amene ankadwala, dzina lake Lazaro. Anali wamʼmudzi wa Betaniya, kwawo kwa Mariya ndi mchemwali wake Marita.+ 2 Mariya ameneyu ndi uja amene anathira Ambuye mafuta onunkhira nʼkupukuta mapazi awo ndi tsitsi lake.+ Lazaro amene ankadwalayu anali mchimwene wake. 3 Choncho azichemwali akewo anatumiza uthenga kwa Yesu kuti: “Ambuye! amene mumamukonda uja akudwala.” 4 Koma Yesu atamva zimenezi ananena kuti: “Kudwala kumeneku si kwa imfa chabe, koma nʼkoti Mulungu alandire ulemerero+ komanso kuti Mwana wa Mulungu alemekezeke chifukwa cha kudwalako.”
5 Yesu ankakonda Marita ndi mchemwali wake komanso Lazaro. 6 Koma atamva kuti Lazaro akudwala, anakhalabe masiku ena awiri kumalo kumene iye anali. 7 Masiku awiriwo atatha, Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Tiyeni tipitenso ku Yudeya.” 8 Ophunzirawo anamuuza kuti: “Rabi,+ posachedwapa Ayudeya amafuna kukugendani ndi miyala,+ ndiye mukufuna kupitanso komweko?” 9 Yesu anayankha kuti: “Kodi masana sali ndi maola 12?+ Munthu akamayenda masana palibe chimamupunthwitsa, chifukwa amaona kuwala kwa dzikoli. 10 Koma munthu akamayenda usiku, amapunthwa chifukwa mwa iye mulibe kuwala.”
11 Atanena zimenezi, anauza ophunzira akewo kuti: “Mnzathu Lazaro ali mʼtulo,+ koma ndikupita kumeneko kukamudzutsa.” 12 Pamenepo ophunzirawo anati: “Ambuye, ngati akugona apeza bwino.” 13 Apa Yesu ankatanthauza kuti Lazaro wamwalira. Koma iwo ankaganiza kuti akunena za kugona tulo teniteni. 14 Kenako Yesu anawauza mosapita mʼmbali kuti: “Lazaro wamwalira,+ 15 ndipo ine ndikusangalala chifukwa cha inu kuti sindinali kumeneko, kuti inu mukhulupirire. Koma tiyeni tipite kwa iye.” 16 Choncho Tomasi, amene ankadziwikanso kuti Didimo, anauza ophunzira anzakewo kuti: “Ifenso tiyeni tipite, kuti tikafere naye limodzi.”+
17 Yesu atafika kumeneko, anapeza kuti Lazaro wakhala ali mʼmanda* masiku 4. 18 Mudzi wa Betaniya unali pafupi ndi Yerusalemu pa mtunda wa makilomita pafupifupi atatu.* 19 Tsopano Ayuda ambiri anabwera kwa Marita ndi Mariya kudzawatonthoza chifukwa cha imfa ya mchimwene wawo. 20 Choncho Marita atamva kuti Yesu akubwera, anapita kukamuchingamira, koma Mariya+ anatsala kunyumba. 21 Marita anauza Yesu kuti: “Ambuye, mukanakhala kuno mchimwene wanga sakanamwalira. 22 Komabe, ngakhale panopa ndikudziwa kuti chilichonse chimene mungapemphe kwa Mulungu, iye adzakupatsani.” 23 Yesu anamuuza kuti: “Mchimwene wako auka.” 24 Marita anati: “Ndikudziwa kuti adzauka pa kuuka kwa akufa+ mʼtsiku lomaliza.” 25 Yesu anamuuza kuti: “Ine ndine kuuka ndi moyo.+ Aliyense wokhulupirira ine, ngakhale atamwalira, adzakhalanso ndi moyo. 26 Komanso aliyense amene ali ndi moyo ndipo amandikhulupirira sadzafa.+ Kodi ukukhulupirira zimenezi?” 27 Iye anayankha kuti: “Inde, Ambuye. Ndimakhulupirira kuti ndinu Khristu Mwana wa Mulungu, amene anthu ankayembekezera kuti adzabwera mʼdzikoli.” 28 Atanena zimenezi, anapita kukaitana mchemwali wake Mariya nʼkumuuza mwachinsinsi kuti: “Mphunzitsi+ wabwera ndipo akukuitana.” 29 Mariya atamva zimenezo, ananyamuka mwamsanga nʼkupita kumene iye anali.
30 Pa nthawiyi nʼkuti Yesu asanalowe mʼmudzimo. Iye anali adakali kumalo kumene Marita anakumana naye. 31 Ayuda amene anali naye pamodzi mʼnyumbamo, amene ankamutonthoza, ataona Mariya akunyamuka mofulumira nʼkutuluka kunja, anamutsatira. Iwo ankaganiza kuti akupita kumanda*+ kukalira kumeneko. 32 Mariya atafika kumene kunali Yesu kuja nʼkumuona, anagwada nʼkuwerama mpaka nkhope yake pansi pafupi ndi mapazi a Yesu. Kenako anamuuza kuti: “Ambuye, mukanakhala kuno mchimwene wanga sakanamwalira.” 33 Yesu atamuona akulira komanso Ayuda amene anabwera naye pamodzi akuliranso, anadzuma povutika mumtima ndi kumva chisoni. 34 Kenako anafunsa kuti: “Mwamuika kuti?” Iwo anati: “Ambuye tiyeni mukaone.” 35 Yesu anagwetsa misozi.+ 36 Pamenepo Ayudawo anayamba kunena kuti: “Taonani, ankamukondadi kwambiri!” 37 Koma ena mwa iwo anati: “Kodi iyeyu, amene anatsegula maso a munthu wakhungu uja,+ sakanatha kuchita chinachake kuti mnzakeyu asamwalire?”
38 Kenako Yesu atadzumanso povutika mumtima, anafika kumandako.* Kwenikweni linali phanga, ndipo analitseka ndi chimwala. 39 Yesu anati: “Chotsani chimwalachi.” Marita, mchemwali wa womwalirayo anauza Yesu kuti: “Ambuye, pano ayenera kuti wayamba kununkha, chifukwa lero ndi tsiku la 4 chimuikireni mʼmanda.” 40 Yesu anamuuza kuti: “Kodi sindinakuuze kuti ngati ungakhulupirire udzaona ulemerero wa Mulungu?”+ 41 Choncho anachotsa chimwalacho. Kenako Yesu anakweza maso ake kumwamba+ nʼkunena kuti: “Atate, ndikukuyamikani kuti mwandimva. 42 Inde, ndikudziwa kuti mumandimva nthawi zonse, koma ndikunena izi chifukwa cha gulu la anthu amene aimirira panowa, kuti akhulupirire kuti inu munandituma ine.”+ 43 Atanena zimenezi, anafuula mokweza mawu kuti: “Lazaro, tuluka!”+ 44 Munthu amene anali wakufa uja anatuluka. Mapazi ndi manja ake anali okulungidwa ndi nsalu zamaliro, nkhope yakenso inali yomanga ndi nsalu. Ndiyeno Yesu anawauza kuti: “Mʼmasuleni kuti athe kuyenda.”
45 Choncho Ayuda ambiri amene anabwera kwa Mariya nʼkuona zimene Yesu anachitazo anamukhulupirira.+ 46 Koma ena a iwo anapita kwa Afarisi kukawauza zimene Yesu anachita. 47 Zitatero ansembe aakulu ndi Afarisi anasonkhanitsa Khoti Lalikulu la Ayuda* nʼkunena kuti: “Kodi tichite chiyani pamenepa? Chifukwatu munthu uyu akuchita zizindikiro zochuluka.+ 48 Ngati titamulekerera, onse adzamukhulupirira ndipo Aroma adzabwera kudzatenga malo* athu ndi mtundu wathu.” 49 Koma mmodzi wa iwo, Kayafa,+ amene anali mkulu wa ansembe chaka chimenecho, anati: “Palibe chimene mukudziwa inu 50 ndipo simukuona kuti nʼzothandiza kwa inu kuti munthu mmodzi afere anthu onse mʼmalo moti mtundu wonse uwonongeke.” 51 Zimene ananenazi, sanaziganize pa iye yekha, koma chifukwa anali mkulu wa ansembe chaka chimenecho, analosera kuti Yesu adzafera mtunduwo. 52 Ndipo osati kufera mtundu chabe, komanso kuti asonkhanitse pamodzi ana a Mulungu amene anamwazikana. 53 Ndipo kuyambira tsiku limenelo anapangana zoti amuphe.
54 Choncho, Yesu sankayendayendanso moonekera kwa Ayuda. Koma anachoka kumeneko nʼkupita kudera lina lapafupi ndi chipululu, mumzinda umene unkatchulidwa kuti Efuraimu.+ Ndipo anakhala kumeneko limodzi ndi ophunzira ake. 55 Tsopano Pasika+ wa Ayuda anali atayandikira ndipo anthu ochuluka anachoka mʼmidzi nʼkupita ku Yerusalemu Pasikayo asanafike, kuti akachite mwambo wa kudziyeretsa. 56 Iwo ankafunafuna Yesu ndipo ankaima pamalo amodzi mʼkachisimo nʼkumakambirana kuti: “Mukuganiza bwanji? Kodi iye uja sabwera kuchikondwererochi?” 57 Koma ansembe aakulu ndi Afarisi analamula kuti aliyense amene angadziwe kumene kuli Yesu, aulule kuti iwo akamugwire.
12 Kutangotsala masiku 6 kuti Pasika ayambike, Yesu anafika ku Betaniya kumene kunali Lazaro,+ amene Yesu anamuukitsa kwa akufa. 2 Choncho anamukonzera chakudya chamadzulo kumeneko ndipo Marita ankawatumikira.+ Lazaro anali mmodzi wa anthu amene ankadya naye. 3 Ndiyeno Mariya anatenga mafuta onunkhira. Mafutawo anali nado weniweni, okwera mtengo kwambiri, okwana magalamu 327.* Mariya anathira mafutawo pamapazi a Yesu nʼkupukuta mapaziwo ndi tsitsi lake. Mʼnyumba monsemo munangoti guu kafungo kabwino ka mafutawo.+ 4 Koma Yudasi Isikariyoti,+ mmodzi wa ophunzira ake, amene anali atatsala pangʼono kumupereka anati: 5 “Nʼchifukwa chiyani mafuta onunkhirawa sanagulitsidwe madinari* 300 nʼkupereka ndalamazo kwa anthu osauka?” 6 Sikuti ananena zimenezi chifukwa ankadera nkhawa osauka, koma chifukwa chakuti anali wakuba. Iye ankasunga bokosi la ndalama ndipo ankaba ndalama zimene zinkaponyedwa mʼbokosilo. 7 Ndiyeno Yesu anawauza kuti: “Musiyeni, achite mwambo umenewu pokonzekera tsiku limene ndidzaikidwe mʼmanda.+ 8 Osaukawo muli nawo nthawi zonse,+ koma ine simudzakhala nane nthawi zonse.”+
9 Kenako gulu lalikulu la Ayuda linadziwa kuti Yesu ali kumeneko. Choncho linafika, osati chifukwa cha Yesu yekha, komanso kuti lidzaone Lazaro, amene iye anamuukitsa kwa akufa.+ 10 Tsopano ansembe aakulu anapangana zoti aphenso Lazaro, 11 chifukwa Ayuda ambiri ankapita kumeneko ndi kukhulupirira Yesu chifukwa cha Lazaroyo.+
12 Tsiku lotsatira, gulu lalikulu la anthu amene anabwera kuchikondwererocho anamva kuti Yesu akubwera ku Yerusalemuko. 13 Choncho anatenga nthambi za kanjedza nʼkutuluka kukamuchingamira. Ndipo anayamba kufuula kuti: “Mʼpulumutseni! Wodalitsidwa ndi amene akubwera mʼdzina la Yehova,*+ amene ndi Mfumu ya Isiraeli!”+ 14 Yesu atapeza bulu wamngʼono, anakwera pabuluyo+ mogwirizana ndi Malemba amene amati: 15 “Usaope mwana wamkazi wa Ziyoni. Taona! Mfumu yako ikubwera itakwera mwana wamphongo wa bulu.”+ 16 Poyamba ophunzira akewo sanathe kumvetsa zimenezi. Koma Yesu atapatsidwa ulemerero,+ iwo anakumbukira kuti zimene anthuwo anamuchitira zinali zofanana ndendende ndi zimene zinalembedwa zokhudza iyeyo.+
17 Tsopano anthu ambiri amene analipo pamene iye anaitana Lazaro kuti atuluke mʼmanda*+ nʼkumuukitsa, anapitiriza kumuchitira umboni.+ 18 Nʼchifukwa chakenso anthu ambiri anapita kukamuchingamira, chifukwa anamva kuti anachita chizindikiro chimenechi. 19 Choncho Afarisi anayamba kukambirana kuti: “Apatu ndiye mukudzionera nokha kuti palibe chimene tikuphulapo. Onani! Dziko lonse likumutsatira.”+
20 Pakati pa anthu amene anabwera kudzalambira kuchikondwereroko panalinso Agiriki. 21 Iwo anapita kwa Filipo+ amene kwawo kunali ku Betsaida wa ku Galileya, ndipo anayamba kumupempha kuti: “Bambo, ife tikufuna tione Yesu.” 22 Filipo anapita kukauza Andireya zimenezo ndipo Andireya ndi Filipo anapita kukauza Yesu.
23 Koma Yesu anawayankha kuti: “Nthawi yakuti Mwana wa munthu alemekezedwe yafika.+ 24 Ndithudi ndikukuuzani, kambewu ka tirigu kakapanda kugwera munthaka nʼkufa, kamakhalabe kamodzi komweko. Koma kakafa+ kamabereka zipatso zambiri. 25 Aliyense amene amakonda moyo wake akuuwononga, koma aliyense amene amadana ndi moyo wake+ mʼdziko lino akuuteteza kuti adzapeze moyo wosatha.+ 26 Ngati munthu akufuna kunditumikira anditsatire ndipo kumene ine ndidzakhale, mtumiki wanga adzakhalanso komweko.+ Aliyense wonditumikira ine, Atate adzamulemekeza. 27 Moyo wanga ukuvutika tsopano,+ kodi ndinene chiyani? Atate ndipulumutseni ku nthawi yovutayi.+ Komabe nthawi imeneyi ikuyenera kundifikira pakuti nʼchifukwa chake ndinabwera. 28 Atate lemekezani dzina lanu.” Atatero mawu+ anamveka kuchokera kumwamba kuti: “Ndalilemekeza ndipo ndidzalilemekezanso.”+
29 Choncho gulu la anthu amene anali ataimirira pamenepo anamva zimenezi ndipo anayamba kunena kuti kwagunda bingu. Ena ankanena kuti: “Mngelo walankhula naye.” 30 Yesu anawauza kuti: “Mawu amenewa sanamveke chifukwa cha ine, koma chifukwa cha inu. 31 Tsopano dziko ili likuweruzidwa, wolamulira wa dzikoli+ aponyedwa kunja tsopano.+ 32 Koma ine ndikadzakwezedwa mʼmwamba padziko lapansi,+ ndidzakokera anthu osiyanasiyana kwa ine.” 33 Ankanena zimenezi pofuna kusonyeza mmene adzafere pakangopita nthawi yochepa.+ 34 Ndiyeno gulu la anthulo linamuyankha kuti: “Ife tinamva mʼChilamulo kuti Khristu adzakhala kosatha.+ Nanga inu mukunena bwanji kuti Mwana wa munthu ayenera kukwezedwa mʼmwamba?+ Kodi Mwana wa munthu ameneyo ndi ndani?” 35 Yesu anawauza kuti: “Kuwala kukhalabe pakati panu kanthawi pangʼono. Yendani pamene kuwalako mudakali nako, kuti mdima usakugwereni. Aliyense amene akuyenda mumdima sadziwa kumene akupita.+ 36 Pamene kuwala mudakali nako, sonyezani kuti mukukhulupirira kuwalako, kuti mukhale ana ake a kuwala.”+
Yesu atanena zimenezi, anachoka nʼkukabisala. 37 Ngakhale kuti anachita zizindikiro zambiri pamaso pawo, iwo sankamukhulupirira, 38 moti mawu a mneneri Yesaya anakwaniritsidwa. Iye anati: “Yehova,* kodi ndi ndani amene wakhulupirira zinthu zimene anamva kwa ife?*+ Ndipo kodi dzanja la Yehova* laonetsedwa kwa ndani?”+ 39 Chifukwa chimene chinachititsa kuti asakhulupirire nʼchimenenso Yesaya ananena kuti: 40 “Wachititsa khungu maso awo ndipo waumitsa mitima yawo, kuti asamaone ndi maso awowo, kuti mitima yawo isamvetse zinthu nʼkutembenuka kuti ine ndiwachiritse.”+ 41 Yesaya ananena zimenezi chifukwa anaona ulemerero wa Khristu, ndipo ananena za iye.+ 42 Komabe panali anthu ena amene anamukhulupirira, ngakhalenso olamulira ambiri.+ Koma sanavomereze poyera, chifukwa ankaopa kuti Afarisi angawachotse musunagoge.+ 43 Iwo ankakonda kwambiri ulemerero wa anthu kuposa ulemerero wa Mulungu.+
44 Koma Yesu anafuula kuti: “Aliyense amene akukhulupirira ine sakukhulupirira ine ndekha, koma akukhulupiriranso amene anandituma.+ 45 Aliyense amene waona ine waonanso amene anandituma.+ 46 Ndabwera monga kuwala mʼdziko,+ kuti aliyense wokhulupirira ine asapitirize kukhala mumdima.+ 47 Ngati munthu wamva mawu anga koma osawasunga, ine sindingamuweruze, chifukwa sindinabwere kudzaweruza dziko, koma kudzalipulumutsa.+ 48 Aliyense wondinyalanyaza komanso wosalandira mawu anga, ali naye mmodzi womuweruza. Mawu amene ine ndalankhula ndi amene adzamuweruze pa tsiku lomaliza. 49 Chifukwa sindinalankhulepo zongoganiza pandekha, koma Atate amene ananditumawo anandipatsa lamulo pa zimene ndiyenera kunena ndi zimene ndiyenera kulankhula.+ 50 Ndipo ndikudziwa kuti lamulo lake ndi lothandiza anthu kudzapeza moyo wosatha.+ Choncho zimene ndimalankhula, ndimazilankhula mogwirizana ndi zimene Atate andiuza.”+
13 Tsopano Yesu anadziwiratu chikondwerero cha Pasika chisanafike kuti nthawi yake yochoka mʼdzikoli kupita kwa Atate+ yakwana.+ Ndipo popeza kuti ankakonda otsatira akewo amene anali mʼdzikoli, anawakonda mpaka pamapeto a moyo wake.+ 2 Chakudya chamadzulo chinali chili mkati ndipo Mdyerekezi anali ataika kale maganizo ofuna kupereka Yesu+ mumtima mwa Yudasi Isikariyoti,+ mwana wa Simoni. 3 Yesu ankadziwa kuti Atate anapereka zinthu zonse mʼmanja mwake komanso kuti anabwera kuchokera kwa Mulungu ndiponso kuti ankapita kwa Mulungu.+ 4 Choncho anaimirira pa chakudya chamadzulocho nʼkuvula malaya ake akunja. Kenako anatenga thaulo nʼkulimanga mʼchiuno mwake.+ 5 Atatero anathira madzi mʼbeseni nʼkuyamba kusambitsa mapazi a ophunzirawo komanso kuwapukuta ndi thaulo limene anamanga mʼchiuno lija. 6 Kenako anafika pa Simoni Petulo. Koma Petulo anafunsa Yesu kuti: “Ambuye, inuyo mukufuna musambitse mapazi anga?” 7 Yesu anayankha kuti: “Zimene ndikuchitazi sungazimvetse panopa, koma pambuyo pake udzamvetsa.” 8 Petulo anati: “Ndithu, sizitheka kuti musambitse mapazi anga.” Yesu anamuyankha kuti: “Ndikapanda kukusambitsa,+ palibe chako kwa ine.” 9 Simoni Petulo anati: “Ambuye, musandisambitse mapazi okha, koma mundisambitsenso manja ndi mutu womwe.” 10 Yesu anamuuza kuti: “Amene wasamba mʼthupi amangofunika kusamba mapazi okha basi, chifukwa thupi lonse ndi loyera. Ndipo inu ndinu oyera, koma osati nonsenu.” 11 Iye ankadziwa munthu amene anakonza zoti amupereke.+ Nʼchifukwa chake ananena kuti: “Sikuti nonsenu ndinu oyera.”
12 Tsopano atasambitsa mapazi awo nʼkuvalanso malaya ake akunja aja, anakhalanso patebulo. Ndiyeno anawafunsa kuti: “Kodi mukudziwa chifukwa chake ndasambitsa mapazi anu? 13 Inu mumanditchula kuti ‘Mphunzitsiʼ komanso ‘Ambuye,’ mumalondola, chifukwa ndinedi Mphunzitsi komanso Ambuye.+ 14 Choncho ngati ine amene ndi Ambuye komanso Mphunzitsi, ndasambitsa mapazi anu,+ inunso mukuyenera kusambitsana mapazi.+ 15 Chifukwa ndakupatsani chitsanzo kuti mmene ine ndachitira kwa inu, inunso muzichita chimodzimodzi.+ 16 Ndithudi ndikukuuzani, kapolo saposa mbuye wake, ndiponso wotumidwa saposa amene wamutuma. 17 Ngati zimenezi mukuzidziwa, mudzakhala osangalala mukamazichita.+ 18 Sindikunena nonsenu, ndikudziwa amene ndawasankha. Koma zimenezi zachitika kuti lemba likwaniritsidwe,+ limene limati: ‘Munthu amene ankadya chakudya changa, watukula chidendene chake nʼkundiukira.’*+ 19 Kuyambira panopa kupita mʼtsogolo, ndizikuuziranitu zisanachitike, kuti zikadzachitika mudzakhulupirire kuti amene munkamuyembekezera uja ndi ine.+ 20 Ndithudi ndikukuuzani, aliyense amene walandira yemwe ine ndamutuma walandiranso ine.+ Ndipo amene walandira ine, walandiranso amene anandituma.”+
21 Atanena zimenezi, Yesu anavutika kwambiri mumtima, ndipo anachitira umboni kuti: “Ndithu ndikukuuzani, mmodzi wa inu andipereka.”+ 22 Ophunzirawo anayamba kuyangʼanizana chifukwa sankadziwa kuti akunena ndani.+ 23 Mmodzi wa ophunzirawo, amene Yesu ankamukonda,+ anakhala pafupi ndi Yesu.* 24 Choncho Simoni Petulo anamugwedezera mutu nʼkumuuza kuti: “Tiuze kuti akunena ndani.” 25 Ndiyeno wophunzira winayo anatsamira pachifuwa pa Yesu nʼkumufunsa kuti: “Ambuye, mukunena ndani?”+ 26 Yesu anayankha kuti: “Ndi amene ndimupatse mkate umene ndisunse.”+ Choncho atasunsa mkatewo, anapatsa Yudasi, mwana wa Simoni Isikariyoti. 27 Yudasi atalandira mkatewo, Satana analowa mwa iye.+ Choncho Yesu anamuuza kuti: “Zimene wakonza kuti uchite, zichite mwamsanga.” 28 Koma pa anthu amene anakhala nawo patebulowo, panalibe aliyense amene anadziwa chifukwa chake anamuuza zimenezo. 29 Popeza Yudasi ankasunga bokosi la ndalama,+ ena ankaganiza kuti Yesu ankamuuza kuti, “Ugule zinthu zonse zimene zikufunikira pachikondwerero,” kapena kuti apereke kenakake kwa osauka. 30 Choncho Yudasi atalandira mkatewo, anatuluka nthawi yomweyo ndipo unali usiku.+
31 Yudasi atatuluka, Yesu anati: “Tsopano Mwana wa munthu walemekezedwa,+ ndipo Mulungu walemekezedwa kudzera mwa iye. 32 Mulungu amulemekeza+ ndipo amulemekeza nthawi yomwe ino. 33 Anzanga apamtima inu,* ndikhala nanu kanthawi kochepa chabe. Mudzandifunafuna, ndipo mogwirizana ndi zimene ndinauza Ayuda aja kuti, ‘Kumene ine ndikupita simungathe kukafikako,’+ tsopano ndikuuzanso inuyo. 34 Ndikukupatsani lamulo latsopano, kuti muzikondana. Mofanana ndi mmene ine ndakukonderani,+ inunso muzikondana choncho.+ 35 Onse adzadziwa kuti ndinu ophunzira anga ngati mukukondana.”+
36 Simoni Petulo anamufunsa kuti: “Ambuye, mukupita kuti?” Yesu anayankha kuti: “Kumene ndikupita sunganditsatire panopa, koma udzanditsatira mʼtsogolo.”+ 37 Petulo anafunsanso kuti: “Ambuye, nʼchifukwa chiyani sindingakutsatireni panopa? Ndidzapereka moyo wanga chifukwa cha inu.”+ 38 Yesu anayankha kuti: “Kodi udzapereka moyo wako chifukwa cha ine? Ndithudi ndikukuuza iwe, tambala asanalire undikana katatu.”+
14 “Mitima yanu isavutike.+ Khulupirirani Mulungu,+ khulupiriraninso ine. 2 Mʼnyumba ya Atate wanga muli malo ambiri okhalamo. Mukanakhala kuti mulibe malo ndikanakuuzani, chifukwa ndikupita kukakukonzerani malo.+ 3 Ndiye ndikapita kukakukonzerani malowo, ndidzabweranso kudzakutengerani kwathu, kuti kumene ine ndikakhale inunso mukakhale komweko.+ 4 Ndipo kumene ine ndikupita, njira yake mukuidziwa.”
5 Tomasi+ anafunsa kuti: “Ambuye, ife sitikudziwa kumene mukupita. Ndiye njira yake tingaidziwe bwanji?”
6 Yesu anamuuza kuti: “Ine ndine njira,+ choonadi+ ndi moyo.+ Palibe amene amafika kwa Atate osadzera mwa ine.+ 7 Anthu inu mukanakhala kuti mukundidziwa, mukanadziwanso Atate wanga. Kuyambira panopa muwadziwa ndipotu mwawaona kale.”+
8 Filipo anamuuza kuti: “Ambuye, tionetseni Atatewo ndipo tikhutira.”
9 Yesu anamuuza kuti: “Kodi iwe Filipo sukundidziwabe ngakhale kuti anthu inu ndakhala nanu nthawi yayitali yonseyi? Amene waona ine waonanso Atate.+ Nanga iwe bwanji ukunena kuti, ‘Tionetseni Atateʼ? 10 Kodi sukukhulupirira kuti Atate ndi ine ndife ogwirizana?+ Zinthu zimene ndimakuuzani sindilankhula zamʼmaganizo mwanga,+ koma Atate amene ndi wogwirizana ndi ine ndi amene akuchita ntchito zake kudzera mwa ine. 11 Khulupirira zimene ndanena kuti ine ndi Atate ndife ogwirizana, apo ayi, ingokhulupirira chifukwa cha ntchito zokhazi.+ 12 Ndithudi ndikukuuzani, aliyense wokhulupirira ine, nayenso adzachita ntchito zimene ine ndimachita, ndipo adzachita ntchito zazikulu kuposa zimenezi+ chifukwa ine ndikupita kwa Atate.+ 13 Komanso chilichonse chimene mudzapemphe mʼdzina langa, ine ndidzachichita, kuti Atate alemekezedwe kudzera mwa Mwana wake.+ 14 Ngati mutapempha chilichonse mʼdzina langa, ine ndidzachichita.
15 Ngati mumandikonda, mudzasunga malamulo anga.+ 16 Ine ndidzapempha Atate ndipo adzakupatsani mthandizi* wina kuti adzakhale nanu mpaka kalekale.+ 17 Mthandizi ameneyo ndi mzimu wa choonadi+ umene dziko silingaulandire, chifukwa siliuona kapena kuudziwa.+ Inu mumaudziwa chifukwa umakhala mwa inu ndipo uli mwa inu. 18 Sindikusiyani ngati ana amasiye. Ndidzabwera kwa inu.+ 19 Kwatsala kanthawi kochepa ndipo dziko silidzandionanso. Koma inu mudzandiona,+ chifukwa ndili ndi moyo ndipo inunso mudzakhala ndi moyo. 20 Pa tsiku limenelo mudzadziwa kuti ine ndi wogwirizana ndi Atate komanso inu ndi ine ndife ogwirizana.+ 21 Aliyense amene ali ndi malamulo anga ndipo amawatsatira, ndi amene amandikonda. Komanso amene amandikonda, Atate wanga adzamukondanso. Inenso ndidzamukonda ndipo ndidzadzionetsera bwinobwino kwa iye.”
22 Yudasi+ wina, osati Isikariyoti, anamufunsa kuti: “Ambuye, nʼchifukwa chiyani mukufuna kudzionetsera bwinobwino kwa ife koma osati kudzikoli?”
23 Yesu anamuyankha kuti: “Ngati munthu amandikonda, adzasunga mawu anga+ ndipo Atate wanga adzamukonda komanso tidzapita kwa iwo nʼkukakhala nawo.+ 24 Amene samandikonda sasunga mawu anga, ndipo mawu amene mukumvawa si anga, koma ndi a Atate amene anandituma.+
25 Ndakuuzani zimenezi pamene ndidakali ndi inu. 26 Koma mthandizi, amene ndi mzimu woyera umene Atate wanga adzatumize mʼdzina langa, adzakuphunzitsani komanso kukukumbutsani zinthu zonse zimene ndinakuuzani.+ 27 Ndikukusiyirani mtendere ndipo ndikupatsani mtendere wanga.+ Sindikuupereka kwa inu ngati mmene dziko limauperekera. Mitima yanu isavutike kapena kuchita mantha. 28 Mwamva ndikukuuzani kuti, ‘Ndikupita ndipo ndidzabweranso kwa inu.’ Ngati mumandikonda, mukanasangalala kuti ndikupita kwa Atate wanga, chifukwa Atate ndi wamkulu kuposa ine.+ 29 Choncho ndakuuzani zisanachitike, kuti zikachitika mukhulupirire.+ 30 Sindilankhula nanu zambiri chifukwa wolamulira wa dziko+ akubwera ndipo alibe mphamvu pa ine.+ 31 Koma kuti dziko lidziwe kuti ndimakonda Atate, ndikuchita zinthu mogwirizana ndi zimene Atatewo anandilamula.+ Nyamukani, tiyeni tichokeko kuno.”
15 “Ine ndine mtengo wa mpesa weniweni ndipo Atate wanga ndi mlimi. 2 Iwo amadula nthambi iliyonse mwa ine imene sikubereka zipatso ndipo iliyonse imene ikubereka zipatso amaiyeretsa poitengulira kuti ibereke zipatso zambiri.+ 3 Inu ndinu oyera kale chifukwa cha mawu amene ine ndakuuzani.+ 4 Mukhale ogwirizana ndi ine ndipo inenso ndikhala wogwirizana ndi inu. Mofanana ndi nthambi imene singabereke zipatso payokha, pokhapokha ngati ili yolumikizikabe kumpesawo, inunso simungabereke zipatso pokhapokha ngati muli olumikizika kwa ine.+ 5 Ine ndine mtengo wa mpesa, inu ndinu nthambi zake. Aliyense amene ali wolumikizika kwa ine, inenso nʼkukhala wolumikizika kwa iye, amabereka zipatso zochuluka+ chifukwa simungathe kuchita chilichonse popanda ine. 6 Ngati munthu sapitiriza kukhala wolumikizika kwa ine, amaponyedwa kunja ngati nthambi ndipo amauma. Anthu amasonkhanitsa nthambi zoterozo nʼkuziponya pamoto ndipo zimapsa. 7 Mukapitiriza kukhala ogwirizana ndi ine ndipo mawu anga akakhala mwa inu, mukhoza kupempha chilichonse chimene mukufuna ndipo chidzachitika kwa inu.+ 8 Atate amalemekezeka mukapitiriza kubereka zipatso zambiri komanso mukamasonyeza kuti ndinu ophunzira anga.+ 9 Mofanana ndi Atate amene amandikonda,+ inenso ndimakukondani. Choncho pitirizani kuchita zinthu zimene zingachititse kuti ndizikukondanibe. 10 Mukamasunga malamulo anga mudzachititsa kuti nthawi zonse ndizikukondani, mofanana ndi ine amene ndimasunga malamulo a Atate nʼkuchititsa kuti nthawi zonse azindikonda.
11 Ndakuuzani zinthu zimenezi kuti mukhale ndi chimwemwe chimene ine ndili nacho komanso kuti chimwemwe chanu chisefukire.+ 12 Ndikukulamulani kuti muzikondana mofanana ndi mmene ine ndimakukonderani.+ 13 Palibe amene ali ndi chikondi chachikulu kuposa cha munthu amene wapereka moyo wake chifukwa cha anzake.+ 14 Mukamachita zimene ndikukulamulani mukhala anzanga.+ 15 Sindikukutchulaninso kuti akapolo chifukwa kapolo sadziwa zimene mbuye wake amachita. Koma ndakutchulani kuti anzanga, chifukwa ndakudziwitsani zinthu zonse zimene ndamva kwa Atate wanga. 16 Si inu amene munandisankha, koma ine ndinakusankhani kuti mupitirize kubereka zipatso zochuluka, komanso kuti zipatso zanuzo zisathe, kuti chilichonse chimene mungapemphe Atate mʼdzina langa akupatseni.+
17 Ndikukulamulani zinthu zimenezi nʼcholinga choti muzikondana.+ 18 Ngati dziko likudana nanu, muzikumbukira kuti linayamba kudana ndi ine lisanadane ndi inu.+ 19 Mukanakhala mbali ya dziko, dziko likanakukondani monga mbali yake. Popeza simuli mbali ya dzikoli,+ koma ine ndinakusankhani kuchokera mʼdziko, pa chifukwa chimenechi dziko likudana nanu.+ 20 Muzikumbukira mawu amene ndinakuuzani aja: Kapolo sangakhale wamkulu kuposa mbuye wake. Ngati anazunza ine, inunso adzakuzunzani.+ Ngati asunga mawu anga, adzasunganso mawu anu. 21 Koma adzakuchitirani zonsezi chifukwa cha dzina langa, chifukwa amene anandituma ine sakumudziwa.+ 22 Ndikanapanda kubwera kudzalankhula nawo, akanakhala opanda tchimo.+ Koma tsopano sangakane tchimo lawo.+ 23 Aliyense amene amadana nane amadananso ndi Atate wanga.+ 24 Ndikanapanda kuchita pamaso pawo ntchito zimene wina aliyense sanachitepo, akanakhala opanda tchimo.+ Koma tsopano andiona ndipo adana nane komanso adana ndi Atate wanga. 25 Zimenezi zachitika kuti mawu amene analembedwa mʼChilamulo akwaniritsidwe. Mawu ake ndi akuti: ‘Anadana nane popanda chifukwa.’+ 26 Akadzafika mthandizi amene ndidzakutumizireni kuchokera kwa Atate, amene ndi mzimu wa choonadi+ wochokera kwa Atate, ameneyo adzandichitira umboni,+ 27 ndipo inunso mudzandichitira umboni,+ chifukwa mwakhala nane kuchokera pachiyambi.”
16 “Ndakuuzani zinthu zimenezi kuti chikhulupiriro chanu chisathe. 2 Anthu adzakuchotsani musunagoge.+ Ndipotu nthawi ikubwera pamene aliyense amene adzakupheni+ adzaganiza kuti wachita utumiki wopatulika kwa Mulungu. 3 Koma adzachita zimenezi chifukwa sakundidziwa komanso sakudziwa Atate.+ 4 Komabe ndakuuzani zinthu zimenezi, kuti nthawi yoti zichitike ikadzafika, mudzakumbukire kuti ndinakuuzani.+
Zinthu zimenezi sindinakuuzeni pachiyambi chifukwa ndinali pamodzi ndi inu. 5 Tsopano ndikupita kwa amene anandituma,+ koma palibe aliyense wa inu amene akundifunsa kuti, ‘Mukupita kuti?’ 6 Koma chifukwa ndakuuzani zinthu zimenezi, chisoni chadzaza mʼmitima yanu.+ 7 Kunena zoona, ndikupita kuti inu mupindule. Chifukwa ngati sindipita ndiye kuti mthandizi uja+ sabwera kwa inu. Koma ndikapita ndikamutumiza kwa inu. 8 Ndipo iye akadzabwera adzapereka umboni wotsimikizika kudzikoli wonena za tchimo, za chilungamo komanso za chiweruzo. 9 Choyamba adzapereka umboni wonena za tchimo,+ chifukwa iwo sakundikhulupirira.+ 10 Kenako adzapereka umboni wonena za chilungamo, chifukwa ine ndikupita kwa Atate ndipo inu simudzandionanso. 11 Pomaliza adzapereka umboni wonena za chiweruzo, chifukwa wolamulira wa dziko lino waweruzidwa.+
12 Ndidakali ndi zinthu zambiri zoti ndikuuzeni, koma panopo simungathe kuzimvetsa zonsezo. 13 Koma mthandiziyo akadzabwera, amene ndi mzimu wa choonadi,+ adzakutsogolerani mʼchoonadi chonse. Chifukwa sadzalankhula zongoganiza payekha, koma adzalankhula zimene wamva ndipo adzalengeza kwa inu zinthu zimene zikubwera.+ 14 Iyeyo adzandilemekeza,+ chifukwa adzalengeza kwa inu zinthu zimene walandira kuchokera kwa ine.+ 15 Zinthu zonse zimene Atate ali nazo ndi zanga.+ Nʼchifukwa chake ndikunena kuti mthandiziyo adzalengeza kwa inu zinthu zimene walandira kuchokera kwa ine. 16 Kwa kanthawi simudzandionanso,+ ndipo kwa kanthawi mudzandiona.”
17 Atanena zimenezi, ena mwa ophunzira akewo anayamba kufunsana kuti: “Kodi akutanthauza chiyani pamene akutiuza kuti, ‘Kwa kanthawi simudzandionanso ndipo kwa kanthawi mudzandiona,’ komanso kuti, ‘chifukwa ndikupita kwa Atateʼ?” 18 Iwo ankanena kuti: “Kodi akutanthauza chiyani pamene akuti, ‘kwa kanthawiʼ? Sitikudziwa zimene akunena.” 19 Yesu anadziwa kuti akufuna kumufunsa, choncho anawafunsa kuti: “Kodi mukufunsana zimenezi chifukwa ndanena kuti: ‘Kwa kanthawi simudzandiona, komanso kuti kwa kanthawi mudzandionaʼ? 20 Ndithudi ndikukuuzani, mudzagwetsa misozi ndi kulira mofuula, koma dzikoli lidzasangalala. Mudzamva chisoni, koma chisoni chanu adzachisandutsa chimwemwe.+ 21 Mayi akamabereka amazunzika kwambiri chifukwa nthawi yake yafika. Koma mwana akabadwa sakumbukiranso kupweteka konse kuja chifukwa chosangalala kuti mwana wabadwa padziko. 22 Chimodzimodzi inunso, panopa muli ndi chisoni. Koma ndidzakuonaninso ndipo mitima yanu idzasangalala.+ Palibenso amene adzachititse kuti musiye kusangalala. 23 Pa tsiku limenelo simudzandifunsanso mafunso. Ndithudi ndikukuuzani, ngati mungapemphe chilichonse kwa Atate+ mʼdzina langa adzakupatsani.+ 24 Mpaka pano simunapemphepo chilichonse mʼdzina langa. Pemphani ndipo mudzalandira kuti chimwemwe chanu chisefukire.
25 Ndalankhula zimenezi kwa inu mʼmafanizo. Nthawi ikubwera pamene sindidzalankhulanso ndi inu pogwiritsa ntchito mafanizo, koma ndidzakuuzani za Atate momveka bwino. 26 Pa tsikulo mudzapempha kanthu kwa Atate mʼdzina langa. Sindikutanthauza kuti ine ndidzakupempherani ayi. 27 Atatewo amakukondani chifukwa munandikonda+ ndipo mwakhulupirira kuti ine ndinabwera monga nthumwi ya Mulungu.+ 28 Ndinabwera padzikoli ngati nthumwi yochokera kwa Atate. Tsopano ndikuchoka mʼdzikoli ndipo ndikupita kwa Atate.”+
29 Ophunzira akewo ananena kuti: “Ambuye, tsopano tikumvetsa zimene mukunena chifukwa simukugwiritsa ntchito mafanizo. 30 Tadziwa tsopano kuti inu mukudziwa zinthu zonse ndipo mʼposafunikanso kuti munthu akufunseni mafunso. Pa chifukwa chimenechi tikukhulupirira kuti munachokeradi kwa Mulungu.” 31 Yesu anawayankha kuti: “Kodi panopa mukukhulupirira? 32 Ndithu ndikukuuzani, nthawi ikubwera ndipo yafika kale, pamene nonse mubalalika, aliyense kupita kunyumba kwake ndipo mundisiya ndekha.+ Koma sindikhala ndekha, chifukwa Atate ali ndi ine.+ 33 Ine ndakuuzani zimenezi kuti mukhale mu mtendere chifukwa cha ine.+ Mʼdzikomu mukumana ndi mavuto aakulu, koma limbani mtima. Ine ndaligonjetsa dziko.”+
17 Yesu atalankhula zinthu zimenezi, anakweza maso ake kumwamba nʼkunena kuti: “Atate, nthawi yafika. Lemekezani mwana wanu, kuti mwana wanu akulemekezeni.+ 2 Inu mwapatsa mwana wanu ulamuliro pa anthu onse+ kuti onse amene inu mwamupatsa,+ awapatse moyo wosatha.+ 3 Moyo wosatha adzaupeza+ akamaphunzira ndi kudziwa za inu, Mulungu yekhayo amene ndi woona,+ komanso za Yesu Khristu, amene inu munamutuma.+ 4 Ndakulemekezani padziko lapansi,+ chifukwa ndamaliza kugwira ntchito imene munandipatsa.+ 5 Ndiye tsopano Atate, ndiloleni kuti ndikhale pambali panu ndipo mundipatse ulemerero umene ndinali nawo pambali panu dziko lisanakhalepo.+
6 Anthu amene munawatenga mʼdziko nʼkundipatsa, ine ndawadziwitsa dzina lanu.+ Anali anu, koma munawapereka kwa ine ndipo iwo amvera mawu anu. 7 Tsopano adziwa kuti zonse zimene munandipatsa nʼzochokera kwa inu, 8 chifukwa mawu amene munandipatsa ndawapereka kwa iwo.+ Iwo awalandira ndipo adziwa ndithu kuti ine ndinabwera ngati nthumwi yanu+ ndipo akhulupirira kuti ndinu amene munandituma.+ 9 Choncho ndikuwapempherera. Sindikupempherera dziko, koma ndikupempherera anthu amene mwandipatsa, chifukwa ndi anu. 10 Zinthu zonse zimene ine ndili nazo ndi zanu ndipo zinthu zanu zonse ndi zanga.+ Ine ndalemekezeka pakati pa anthu amene mwandipatsa.
11 Ine sindipitiriza kukhala mʼdzikoli chifukwa ndikubwera kwa inu, koma iwowo adakali mʼdzikoli.+ Atate Woyera, ayangʼanireni+ chifukwa cha dzina lanu limene mwandipatsa, kuti akhale amodzi* ngati mmene ife tilili.+ 12 Pamene ndinali nawo limodzi, ndinkawayangʼanira+ chifukwa cha dzina lanu limene mwandipatsa. Ine ndawateteza moti palibe aliyense wa iwo amene wawonongeka+ kupatulapo mwana wa chiwonongeko,+ kuti lemba likwaniritsidwe.+ 13 Koma tsopano ndikubwera kwa inu, ndipo ndikulankhula zimenezi pamene ndili mʼdziko kuti iwo akhale ndi chimwemwe chosefukira ngati chimene ine ndili nacho.+ 14 Iwo ndawapatsa mawu anu, koma dziko likudana nawo chifukwa sali mbali ya dziko,+ mofanana ndi ine amene sindili mbali ya dziko.
15 Sindikupempha kuti muwachotse mʼdziko, koma kuti muwateteze kwa woipayo.+ 16 Iwo sali mbali ya dziko,+ mofanana ndi ine amenenso sindili mbali ya dziko.+ 17 Ayeretseni* pogwiritsa ntchito choonadi.+ Mawu anu ndi choonadi.+ 18 Inu munanditumiza ine mʼdziko. Mofanana ndi zimenezi, inenso ndawatumiza mʼdziko.+ 19 Ndipo ine ndikudziyeretsa chifukwa cha iwo, kuti iwonso ayeretsedwe ndi choonadi.
20 Sindikupempherera awa okha, koma ndikupemphereranso amene amakhulupirira ine atamvetsera zimene iwo amaphunzitsa. 21 Ndikuchita zimenezi kuti onsewa akhale amodzi+ ngati mmene inu Atate ndi ine tilili ogwirizana,+ kuti iwonso akhale ogwirizana ndi ife nʼcholinga choti dziko likhulupirire kuti inu munanditumadi. 22 Ndawapatsa ulemerero umene munandipatsa, kuti iwo akhale amodzi ngati mmene ifenso tilili amodzi.+ 23 Ine ndikhale wogwirizana ndi iwo, inu mukhale wogwirizana ndi ine, kuti iwo akhale mumgwirizano weniweni,* kuti dziko lidziwe kuti inu munandituma ine komanso kuti mumawakonda ngati mmene mumandikondera ine. 24 Atate, ine ndikufuna kuti amene mwandipatsawa adzakhale limodzi ndi ine kumene ine ndidzakhale,+ kuti adzaone ulemerero wanga umene inu mwandipatsa, chifukwa munandikonda musanayale maziko a dziko.+ 25 Atate Wolungama, ndithudi dziko silikukudziwani,+ koma ine ndikukudziwani+ ndipo awa adziwa kuti inu munandituma. 26 Ine ndachititsa kuti iwo adziwe dzina lanu ndipo ndidzapitiriza kuwadziwitsa dzinalo+ kuti iwonso azisonyeza chikondi ngati chimene inu munandisonyeza, kuti inenso ndikhale wogwirizana ndi iwo.”+
18 Atamaliza kunena zinthu zimenezi, Yesu anatuluka limodzi ndi ophunzira ake nʼkuwoloka chigwa cha Kidironi+ kupita kumene kunali munda. Iye ndi ophunzira akewo analowa mʼmundamo.+ 2 Yudasi amene anamupereka uja, ankawadziwanso malowo chifukwa nthawi zambiri Yesu ankakumana ndi ophunzira ake kumeneko. 3 Choncho Yudasi anatenga gulu la asilikali komanso alonda ochokera kwa ansembe aakulu ndi kwa Afarisi. Iwo anafika kumeneko atanyamula miyuni, nyale ndi zida.+ 4 Popeza Yesu ankadziwa zonse zimene zimuchitikire, anawayandikira nʼkuwafunsa kuti: “Mukufuna ndani?” 5 Iwo anamuyankha kuti: “Yesu Mnazareti.”+ Iye anati: “Ndi ineyo.” Yudasi amene anamupereka uja, analinso pomwepo.+
6 Koma pamene anawauza kuti: “Ndi ineyo,” iwo anabwerera mʼmbuyo nʼkugwa pansi.+ 7 Kenako anawafunsanso kuti: “Mukufuna ndani?” Iwo anati: “Yesu Mnazareti.” 8 Yesu anati: “Ndakuuzani kuti ndi ineyo. Choncho ngati mukufuna ine, awa asiyeni azipita.” 9 Zimenezi zinachitika kuti mawu amene iye ananena akwaniritsidwe akuti: “Pa anthu onse amene munandipatsa sindinatayepo ngakhale mmodzi.”+
10 Kenako Simoni Petulo, amene anali ndi lupanga, analisolola nʼkutema nalo kapolo wa mkulu wa ansembe mpaka kuduliratu khutu lake lakumanja.+ Kapoloyo dzina lake anali Makasi. 11 Koma Yesu anauza Petulo kuti: “Bwezera lupangalo mʼchimake.+ Kodi sindiyenera kumwa zamʼkapu imene Atate wandipatsa?”+
12 Kenako asilikali aja, mkulu wa asilikali ndi alonda a Ayuda anagwira Yesu nʼkumumanga. 13 Choyamba anapita naye kwa Anasi, chifukwa anali mpongozi wa Kayafa,+ amene anali mkulu wa ansembe chaka chimenecho.+ 14 Kayafa ameneyu ndi amene analangiza Ayuda uja kuti zinali zothandiza kwa iwo kuti munthu mmodzi afere anthu onse.+
15 Ndiyeno Simoni Petulo komanso wophunzira wina ankatsatira Yesu.+ Wophunzira winayo ankadziwana ndi mkulu wa ansembe, choncho analowa limodzi ndi Yesu mʼbwalo lapanyumba ya mkulu wa ansembe. 16 Koma Petulo anaima kunja pakhomo. Choncho wophunzira amene ankadziwana ndi mkulu wa ansembe uja, anapita kukalankhula ndi mlonda wapakhomo nʼkumulowetsa Petulo. 17 Mtsikana wantchito amene anali mlonda wa pakhomopo anafunsa Petulo kuti: “Kodi inunso si mmodzi wa ophunzira a munthu ameneyu?” Iye anati: “Ayi si ine.”+ 18 Ndiyeno akapolo ndi alonda anali ataima chapafupi ndi moto wamakala umene anakoleza, chifukwa kunkazizira ndipo ankawotha motowo. Nayenso Petulo anaima nawo limodzi nʼkumawotha motowo.
19 Ndiyeno wansembe wamkulu anafunsa Yesu za ophunzira ake komanso zimene ankaphunzitsa. 20 Yesu anamuyankha kuti: “Ndalankhula poyera ku dzikoli. Nthawi zonse ndinkaphunzitsa mʼmasunagoge ndi mʼkachisi,+ kumene Ayuda onse ankasonkhana, ndipo sindinalankhule chilichonse kumbali. 21 Nʼchifukwa chiyani mukufunsa ine? Funsani amene anamva zimene ndinkawauza. Onani! Onsewa akudziwa zimene ndinanena.” 22 Atanena zimenezi, mmodzi wa alonda amene anaima chapafupi anamenya Yesu mbama+ nʼkunena kuti: “Ungamuyankhe choncho wansembe wamkulu?” 23 Yesu anamuyankha kuti: “Ngati ndanena chilichonse cholakwika, pereka umboni wa cholakwikacho. Koma ngati zimene ndanenazi ndi zoona, nʼchifukwa chiyani wandimenya?” 24 Kenako Anasi anatumiza Yesu kwa Kayafa mkulu wa ansembe ndipo anali atamumanga.+
25 Pa nthawiyi Simoni Petulo anali ataima pomwepo nʼkumawotha moto. Ndiyeno iwo anamufunsa kuti: “Kodi iwenso si mmodzi wa ophunzira ake?” Iye anakana nʼkunena kuti: “Ayi si ine.”+ 26 Mmodzi wa akapolo a mkulu wa ansembe, amenenso anali wachibale wa munthu amene Petulo anamudula khutu uja,+ anati: “Ndinakuona mʼmunda muja uli naye limodzi, ndikunama kapena?” 27 Koma Petulo anakananso ndipo nthawi yomweyo tambala analira.+
28 Ndiyeno iwo anatenga Yesu kuchoka kwa Kayafa nʼkupita naye kunyumba ya bwanamkubwa.+ Umenewu unali mʼmawa kwambiri. Koma iwo sanalowe mʼnyumba ya bwanamkubwayo poopa kudetsedwa.+ Iwo ankafuna kuti akathe kudya Pasika. 29 Choncho Pilato anatuluka nʼkuwafunsa kuti: “Kodi mukumuimba mlandu wanji munthu ameneyu?” 30 Iwo anamuyankha kuti: “Munthuyu akanakhala kuti sachita zoipa,* sitikanabwera naye kwa inu.” 31 Ndiyeno Pilato anawauza kuti: “Mutengeni mukamuweruze nokha mogwirizana ndi chilamulo chanu.”+ Ayudawo anamuuza kuti: “Tilibe ulamuliro wopha munthu aliyense.”+ 32 Zimenezi zinachitika kuti mawu amene Yesu ananena osonyeza mmene adzafere, akwaniritsidwe.+
33 Choncho Pilato analowanso mʼnyumba ya bwanamkubwa nʼkuitana Yesu ndipo anamufunsa kuti: “Kodi ndiwe Mfumu ya Ayuda?”+ 34 Yesu anayankha kuti: “Kodi mukufunsa zimenezi chifukwa mukufunadi kudziwa, kapena chifukwa chakuti ena akuuzani za ine?” 35 Pilato anayankha kuti: “Kodi ine ndine Myuda ngati? Anthu a mtundu wako omwe komanso ansembe aakulu ndi amene akupereka kwa ine. Kodi unachita chiyani?” 36 Yesu anayankha kuti:+ “Ufumu wanga si wamʼdzikoli.+ Ufumu wanga ukanakhala wamʼdzikoli, atumiki anga akanamenya nkhondo kuti ndisaperekedwe kwa Ayuda.+ Koma Ufumu wanga si wochokera mʼdzikoli.” 37 Pilato anamufunsa kuti: “Chabwino, koma kodi ndiwe mfumu?” Yesu anayankha kuti: “Mukunena nokha kuti ndine mfumu.+ Ndinabadwa komanso ndinabwera mʼdziko kuti ndidzachitire umboni choonadi.+ Aliyense amene ali kumbali ya choonadi amamvetsera mawu anga.” 38 Pilato anamufunsa kuti: “Choonadi nʼchiyani?”
Atangofunsa funso limeneli anatuluka nʼkupitanso kumene kunali Ayuda kuja, ndipo anawauza kuti: “Ineyo sindikupeza cholakwa chilichonse mwa munthu ameneyu.+ 39 Pajanso inu muli ndi mwambo wakuti ndizikumasulirani munthu mmodzi pa Pasika.+ Ndiye kodi mukufuna kuti ndikumasulireni Mfumu ya Ayuda?” 40 Anthuwo anafuulanso kuti: “Ameneyo ayi, koma Baraba!” Komatu Baraba ameneyu anali wachifwamba.+
19 Kenako Pilato anatenga Yesu nʼkumukwapula.+ 2 Ndipo asilikali analuka chisoti chachifumu chaminga nʼkumuveka kumutu. Anamuvekanso malaya akunja apepo.+ 3 Ndiye ankapita kwa iye nʼkumanena kuti: “Moni, inu Mfumu ya Ayuda!” Komanso ankamumenya makofi kumaso.+ 4 Pilato anatulukanso kunja nʼkuwauza kuti: “Onani! ndimutulutsa panja pano kwa inu, kuti mudziwe kuti sindinamupeze ndi mlandu.”+ 5 Choncho Yesu anatuluka panja atavala chisoti chachifumu chaminga chija ndi malaya akunja apepo. Ndiyeno Pilato anawauza kuti: “Taonani! Mwamuna uja ndi uyu!” 6 Koma pamene ansembe aakulu ndi alonda anamuona, anafuula kuti: “Apachikidwe ameneyo! Apachikidwe ameneyo!”*+ Pilato anawauza kuti: “Mutengeni mukamupachike nokha,* chifukwa ine sindinamupeze ndi mlandu uliwonse.”+ 7 Ayudawo anamuyankha kuti: “Tili ndi chilamulo ife, ndipo malinga ndi chilamulocho iyeyu akuyenera kufa+ chifukwa akudziyesa mwana wa Mulungu.”+
8 Pilato atamva zimene ananenazo, anachita mantha kwambiri, 9 ndiye analowanso mʼnyumba ya bwanamkubwa muja nʼkufunsa Yesu kuti: “Kodi umachokera kuti?” Koma Yesu sanamuyankhe.+ 10 Ndiyeno Pilato anamuuza kuti: “Kodi sukufuna kulankhula nane? Kodi sukudziwa kuti ndili ndi mphamvu zokumasula komanso zokupachika?”* 11 Yesu anamuyankha kuti: “Simukanakhala ndi mphamvu iliyonse pa ine mukanapanda kupatsidwa kuchokera kumwamba. Nʼchifukwa chake munthu amene wandipereka kwa inu ali ndi tchimo lalikulu kwambiri.”
12 Chifukwa cha zimenezi Pilato anayesetsabe kufunafuna njira yoti amumasulire. Koma Ayudawo anafuula kuti: “Mukamumasula munthu ameneyu, ndiye kuti si inu mnzake wa Kaisara. Munthu aliyense amene amadziyesa mfumu ndi wotsutsana ndi Kaisara.”+ 13 Ndiye Pilato atamva mawu amenewa, anatulutsa Yesu panja, ndipo iye anakhala pampando woweruzira milandu, pamalo amene ankatchulidwa kuti Bwalo Lamiyala, koma pa Chiheberi ankatchulidwa kuti Gabʹba·tha. 14 Tsiku limeneli linali Tsiku Lokonzekera+ Pasika ndipo nthawi inali cha mʼma 12 koloko masana.* Ndiyeno iye anauza Ayudawo kuti: “Taonani! Mfumu yanu imeneyi!” 15 Koma iwo anafuula kuti: “Muthane naye! Muthane naye! Apachikidwe ameneyo!”* Pilato anawafunsa kuti: “Kodi ndipachike mfumu yanu?” Ansembe aakulu anayankha kuti: “Tilibe mfumu ina koma Kaisara.” 16 Kenako anamupereka kwa iwo kuti akamuphe pomupachika pamtengo.+
Tsopano Yesu anali mʼmanja mwawo. 17 Iye ananyamula yekha mtengo wozunzikirapo* nʼkutuluka kupita kumalo amene ankatchulidwa kuti Chibade,+ koma pa Chiheberi ankatchulidwa kuti Gologota.+ 18 Kumeneko anamupachika pamtengo+ limodzi ndi amuna ena awiri, wina mbali iyi, wina mbali inayi, Yesu pakati.+ 19 Pilato analembanso dzina laudindo nʼkuliika pamtengo wozunzikirapowo.* Analemba kuti: “Yesu Mnazareti, Mfumu ya Ayuda.”+ 20 Ayuda ambiri anawerenga dzina laudindo limeneli, chifukwa malo amene Yesu anapachikidwawo anali pafupi ndi mzinda, ndipo analilemba mʼChiheberi, mʼChilatini ndi mʼChigiriki. 21 Koma ansembe aakulu a Ayudawo anauza Pilato kuti: “Musalembe kuti ‘Mfumu ya Ayuda,’ koma mulembe kuti iye ananena kuti, ‘Ndine Mfumu ya Ayuda.’” 22 Koma Pilato anawayankha kuti: “Zimene ndalemba, ndalemba.”
23 Asilikaliwo atamukhomerera Yesu pamtengo, anatenga malaya ake akunja nʼkuwagawa zigawo 4, kuti msilikali aliyense atenge chigawo chimodzi. Anatenganso malaya amkati. Koma malaya amkatiwo analibe msoko, anawombedwa kuchokera pamwamba mpaka pansi. 24 Choncho iwo anakambirana kuti: “Malayawa tisawangʼambe, koma tiyeni tichite maere kuti tidziwe amene angatenge malaya amenewa.”+ Zimenezi zinachitika kuti lemba likwaniritsidwe, limene limati: “Iwo anagawana zovala zanga, ndipo anachita maere pa zovala zanga.”+ Choncho asilikaliwo anachitadi zimenezi.
25 Koma chapafupi ndi mtengo wozunzikirapo* wa Yesu, panaima mayi ake+ ndi mchemwali wa mayi akewo, Mariya mkazi wa Kulopa, komanso Mariya wa ku Magadala.+ 26 Choncho Yesu ataona mayi akewo ndi wophunzira amene ankamukonda uja+ ataima chapafupi, anauza mayi akewo kuti: “Mayi, kuyambira lero, uyu akhala mwana wanu.” 27 Kenako anauza wophunzirayo kuti: “Kuyambira lero awa akhala mayi ako.” Kuyambira nthawi imeneyo wophunzirayo anatenga mayiwo nʼkupita nawo kunyumba kwake.
28 Pambuyo pake, Yesu atadziwa kuti tsopano zonse zachitika, kuti malemba akwaniritsidwe ananena kuti: “Ndikumva ludzu.”+ 29 Pamalopo panali mtsuko wodzaza vinyo wowawasa. Choncho anatenga siponji nʼkuiviika muvinyo wowawasayo ndipo anaisomeka kukamtengo ka hisope* nʼkuifikitsa pakamwa pake.+ 30 Atalandira vinyo wowawasayo, Yesu anati: “Ndakwaniritsa chifuniro chanu!”+ ndipo anaweramitsa mutu nʼkupereka mzimu wake.*+
31 Popeza linali Tsiku Lokonzekera,+ Ayudawo sanafune kuti mitembo ikhalebe pamitengo yozunzikirapo+ tsiku la Sabata, (chifukwa Sabata la tsiku limeneli linali lalikulu),+ ndiye iwo anapempha Pilato kuti awalole kuti athyole miyendo ya anthu amene anapachikidwawo nʼkutsitsa mitembo yawo. 32 Choncho asilikali anabwera nʼkuthyola miyendo ya munthu woyamba ndiponso ya wina uja amene anapachikidwa naye limodzi. 33 Koma atafika pa Yesu, anapeza kuti wafa kale ndiye sanamuthyole miyendo. 34 Koma mmodzi wa asilikaliwo anamubaya ndi mkondo munthiti+ ndipo nthawi yomweyo panatuluka magazi ndi madzi. 35 Munthu amene anaona zimenezo ndi amene wapereka umboni umenewu ndipo umboni wakewo ndi woona. Iye akudziwa kuti amanena zoona, kuti inunso mukhulupirire.+ 36 Kwenikweni zimenezi zinachitika kuti lemba likwaniritsidwe, limene limati: “Sadzathyola* fupa lake ndi limodzi lomwe.”+ 37 Ndiponso lemba lina limati: “Iwo adzayangʼana kwa munthu amene anamubaya.”+
38 Pambuyo pa zinthu zimenezi, Yosefe wa ku Arimateya, amene anali wophunzira wachinsinsi wa Yesu chifukwa ankaopa Ayuda,+ anapempha Pilato kuti akachotse mtembo wa Yesu ndipo Pilato anamupatsa chilolezo. Choncho anafika nʼkuchotsa mtembowo.+ 39 Nikodemo+ amene anabwera kwa iye usiku poyamba paja, anabweranso atatenga mule wosakaniza ndi aloye, wopitirira makilogalamu 32.*+ 40 Choncho iwo anatenga mtembo wa Yesu nʼkuukulunga ndi nsalu zamaliro zonunkhira,+ mogwirizana ndi mwambo umene Ayuda ankatsatira poika maliro. 41 Tsopano kumalo kumene anamupachikirako kunali munda mmene munali manda* atsopano,+ ndipo anali asanaikemo munthu chiyambire. 42 Popeza linali Tsiku Lokonzekera+ Chikondwerero cha Ayuda, ndipo mandawo anali pafupi, iwo anaika Yesu mmenemo.
20 Tsiku loyamba la mlunguwo, Mariya wa ku Magadala anapita kumandako* mʼmawa kwambiri,+ kudakali mdima, ndipo anaona kuti mwala wachotsedwa kale pamandawo.*+ 2 Choncho anathamanga kupita kwa Simoni Petulo ndi kwa wophunzira wina, amene Yesu ankamukonda kwambiri uja.+ Iye anawauza kuti: “Ambuye awachotsa mʼmanda*+ muja, ndipo sitikudziwa kumene awaika.”
3 Atatero Petulo ndi wophunzira wina uja ananyamuka kupita kumandako. 4 Onse awiri anayambira limodzi kuthamanga, koma wophunzira winayo ankathamanga kwambiri kuposa Petulo ndipo anali woyambirira kukafika kumandako. 5 Atawerama nʼkusuzumira mkatimo, anaona nsalu zili pansi,+ koma sanalowemo. 6 Kenako Simoni Petulo amene ankabwera mʼmbuyo mwake anafikanso, ndipo analowa mʼmandamo. Mmenemo anaona nsalu zija zili pansi. 7 Nsalu imene anamukulungira kumutu sinaikidwe pamodzi ndi nsalu zina zija, koma anaipindapinda nʼkuiika payokha. 8 Kenako wophunzira amene anayambirira kufika kumanda uja analowanso mkatimo, ndipo anaona nʼkukhulupirira zimene anauzidwa. 9 Iwo anali asanamvetse zimene malemba amanena kuti Yesu ayenera kuuka kwa akufa.+ 10 Choncho ophunzirawo anabwerera kunyumba kwawo.
11 Koma Mariya anatsala atangoima panja pafupi ndi mandawo, akulira. Akulira choncho, anawerama kuti aone mʼmandamo 12 ndipo anaona angelo awiri+ amene anavala zoyera atakhala pamene panali mtembo wa Yesu. Mmodzi anakhala pansi kumutu ndipo wina anakhala kumiyendo. 13 Iwo anamufunsa kuti: “Mayi, nʼchifukwa chiyani mukulira?” Mayiwo anawayankha kuti: “Atenga Ambuye wanga, ndipo sindikudziwa kumene awaika.” 14 Atanena zimenezi, anatembenuka ndipo anaona Yesu ataima pamenepo, koma sanamuzindikire kuti ndi Yesu.+ 15 Yesu anafunsa mayiyo kuti: “Mayi iwe, nʼchifukwa chiyani ukulira? Kodi ukufuna ndani?” Poganiza kuti ndi amene ankasamalira mundawo, iye anamuyankha kuti: “Bambo, ngati mwamuchotsa ndinu, ndiuzeni chonde kumene mwamuika ndipo ine ndikamutenga.” 16 Yesu anamuuza kuti: “Mariya!” Iye anatembenuka nʼkumuuza mʼChiheberi kuti: “Rab·boʹni!” (kutanthauza kuti “Mphunzitsi!”) 17 Yesu anamuuza kuti: “Usandikangamire chifukwa nthawi yoti ndipite kwa Atate sinakwane. Koma pita kwa abale anga+ ndipo ukawauze kuti, ‘Ine ndikupita kwa Atate wanga+ ndi Atate wanu, kwa Mulungu wanga+ ndi Mulungu wanu.’” 18 Mariya wa ku Magadala anapita kwa ophunzirawo ndipo anawauza kuti: “Ambuye ndawaona ine!” Ndipo anawauza zimene Yesu anamuuza zija.+
19 Madzulo a tsiku limenelo, limene linali tsiku loyamba la mlungu, ophunzirawo anasonkhana pamodzi. Mʼnyumba imene anasonkhanayo anakhoma zitseko chifukwa ankaopa Ayuda. Koma Yesu analowa nʼkuima pakati pawo ndipo anawauza kuti: “Mtendere ukhale nanu.”+ 20 Atanena zimenezi, anawaonetsa manja ake ndi munthiti mwake.+ Choncho ophunzirawo anasangalala ataona Ambuyewo.+ 21 Yesu anawauzanso kuti: “Mtendere ukhale nanu.+ Mofanana ndi mmene Atate ananditumira,+ inenso ndikukutumani.”+ 22 Atanena zimenezi, anauzira mpweya pa iwo nʼkuwauza kuti: “Landirani mzimu woyera.+ 23 Mukakhululukira munthu amene wachita tchimo, ndiye kuti Mulungu wamukhululukira kale. Koma mukapanda kukhululukira munthu amene wachita tchimo, ndiye kuti Mulungu sanamukhululukire.”
24 Koma Tomasi,+ amene ankadziwikanso kuti Didimo, mmodzi wa ophunzira 12 aja sanali nawo limodzi pamene Yesu anabwera. 25 Choncho ophunzira enawo anamuuza kuti: “Ife tawaona Ambuye!” Koma iye anawayankha kuti: “Ndikapanda kuona mabala a misomali mʼmanja mwawo ndi kuika chala changa mʼmabala a misomaliwo ndiponso kuika dzanja langa munthiti mwawo,+ ndithu ine sindikhulupirira.”
26 Patapita masiku 8, ophunzira akewo analinso mʼnyumba ndipo Tomasi anali nawo limodzi. Yesu analowa ngakhale kuti zitseko zinali zokhoma ndipo anaimirira pakati pawo nʼkunena kuti: “Mtendere ukhale nanu.”+ 27 Kenako anauza Tomasi kuti: “Ika chala chako apa ndiponso ona mʼmanja mwangamu. Bweretsa dzanja lako ugwire munthiti mwangamu ndipo usiye kukayikira* koma ukhulupirire.” 28 Tomasi anayankha kuti: “Mbuyanga komanso Mulungu wanga!” 29 Yesu anamufunsa kuti: “Kodi wakhulupirira chifukwa wandiona? Osangalala ndi amene amakhulupirira ngakhale asanaone.”
30 Kunena zoona, Yesu anachitanso zizindikiro zina zambiri pamaso pa ophunzirawo, zimene sizinalembedwe mumpukutu uno.+ 31 Koma izi zalembedwa kuti mukhulupirire kuti Yesu ndi Khristu, Mwana wa Mulungu, komanso chifukwa choti mwakhulupirira, mukhale ndi moyo mʼdzina lake.+
21 Zimenezi zitatha, Yesu anaonekeranso kwa ophunzirawo kunyanja ya Tiberiyo.* Kuonekera kwakeko kunali motere. 2 Simoni Petulo, Tomasi (amene ankatchulidwa kuti Didimo),+ Natanayeli+ wa ku Kana wa ku Galileya, ana a Zebedayo+ ndi ophunzira ake ena awiri onsewa anali pamodzi. 3 Ndiyeno Simoni Petulo anati: “Ine ndikupita kukapha nsomba.” Enawonso anati: “Ifenso tipita nawe.” Iwo anapitadi nʼkukwera ngalawa, koma mkati mwa usiku umenewo sanaphe kanthu.+
4 Koma pamene kunkacha, Yesu anaimirira mʼmbali mwa nyanja, koma ophunzirawo sanazindikire kuti anali Yesu.+ 5 Kenako Yesu anati: “Ana inu, kodi muli ndi chakudya chilichonse?”* Iwo anamuyankha kuti, “Ayi!” 6 Iye anawauza kuti: “Ponyani ukonde kumbali yakudzanja lamanja kwa ngalawayo ndipo mupeza kenakake.” Choncho anaponyadi ukondewo, koma sanathenso kuukokera mungalawa chifukwa cha kuchuluka kwa nsomba.+ 7 Zitatero, wophunzira amene Yesu ankamukonda kwambiri uja+ anauza Petulo kuti: “Ndi Ambuye!” Simoni Petulo atamva kuti ndi Ambuye, anavala malaya ake akunja, chifukwa anali maliseche,* ndipo analumphira mʼnyanja. 8 Koma ophunzira enawo anabwera mʼngalawa yaingʼono akukoka ukonde wodzaza ndi nsomba, chifukwa sanali patali kwenikweni ndi kumtunda. Anali pa mtunda wa mamita pafupifupi 90 okha.*
9 Atafika kumtunda anaona moto wamakala ndipo panali nsomba komanso anaona mkate. 10 Yesu anawauza kuti: “Bweretsani kuno zina mwa nsomba zimene mwaphazo.” 11 Choncho Simoni Petulo analowa mʼngalawamo nʼkukokera kumtunda ukonde wodzaza nsomba zikuluzikulu zokwana 153. Koma ngakhale kuti munali nsomba zochuluka choncho, ukondewo sunangʼambike. 12 Yesu anawauza kuti: “Bwerani mudzadye chakudya chamʼmawa.” Panalibe ngakhale mmodzi mwa ophunzirawo amene analimba mtima kumufunsa kuti: “Ndinu ndani?” chifukwa ankadziwa kuti ndi Ambuye. 13 Yesu anapita kukatenga mkate nʼkuwagawira, ndipo anachitanso chimodzimodzi ndi nsomba. 14 Kameneka kanali kachitatu+ kuti Yesu aonekere kwa ophunzira akewo pambuyo poti waukitsidwa kwa akufa.
15 Atamaliza kudya chakudya chamʼmawacho, Yesu anafunsa Simoni Petulo kuti: “Simoni mwana wa Yohane, kodi umandikonda ine kuposa izi?” Iye anamuyankha kuti: “Inde Ambuye, inunso mukudziwa kuti ndimakukondani kwambiri.” Iye anamuuza kuti: “Dyetsa ana a nkhosa anga.”+ 16 Kenako anamufunsa kachiwiri kuti: “Simoni mwana wa Yohane, kodi ine umandikonda?” Iye anamuyankha kuti: “Inde Ambuye, inunso mukudziwa kuti ndimakukondani kwambiri.” Pamenepo anati: “Weta ana a nkhosa anga.”+ 17 Anamufunsanso kachitatu kuti: “Simoni mwana wa Yohane, kodi ine umandikonda kwambiri?” Petulo anamva chisoni kuti akumufunsa kachitatu kuti: “Kodi ine umandikonda kwambiri?” Choncho iye anati: “Ambuye, inu mumadziwa zinthu zonse. Mukudziwanso bwino kuti ndimakukondani kwambiri.” Yesu anamuuza kuti: “Dyetsa ana a nkhosa anga.+ 18 Ndithudi ndikukuuza iwe, pamene unali mnyamata, unkavala wekha nʼkupita kumene ukufuna. Koma ukadzakalamba, udzatambasula manja ako ndipo munthu wina adzakuveka ndipo adzakunyamula nʼkupita nawe kumene iwe sukufuna.” 19 Ananena zimenezi pofuna kusonyeza mtundu wa imfa imene adzalemekeze nayo Mulungu. Atanena zimenezi, anamuuza kuti: “Pitiriza kunditsatira.”+
20 Petulo anatembenuka nʼkuona wophunzira amene Yesu ankamukonda uja+ akuwatsatira. Wophunzira ameneyu ndi amene pa chakudya chamadzulo chija anatsamira pachifuwa cha Yesu nʼkumufunsa kuti: “Ambuye, ndi ndani amene akufuna kukuperekani?” 21 Choncho atamuona, Petulo anafunsa Yesu kuti: “Ambuye, nanga uyu adzachita chiyani?” 22 Yesu anati: “Ngati ine nditafuna kuti akhalebe ndi moyo mpaka ndidzabwere, kodi iweyo zikukukhudza bwanji? Iweyo ungopitiriza kunditsatira.” 23 Choncho zinamveka pakati pa abale kuti wophunzira ameneyu sadzamwalira. Komabe Yesu sanamuuze kuti sadzamwalira, koma ananena kuti: “Ngati ine nditafuna kuti akhalebe ndi moyo mpaka ndidzabwere, kodi iweyo zikukukhudza bwanji?”
24 Wophunzira ameneyu+ ndi amene akuchitira umboni zinthu zimenezi. Iyeyu ndi amenenso analemba zinthu zimenezi ndipo tikudziwa kuti umboni umene akupereka ndi woona.
25 Pali zinthu zinanso zambiri zimene Yesu anachita. Zikanakhala kuti zonse zinalembedwa mwatsatanetsatane, ndikuganiza kuti mipukutu yolembedwayo sikanakwana mʼdzikoli.+
Kapena kuti, “anali ngati mulungu.”
Kapena kuti, “ankamusonyeza kukoma mtima kwakukulu.”
Kapena kuti, “pachifuwa cha Atate.” Izi zikusonyeza kuti ankakondedwa mwapadera.
Onani Zakumapeto A5.
Kapena kuti, “mwangamu wandipitirira.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ola la 10,” kuwerenga kuchokera mʼma 6 koloko mʼmawa.
Amenewa ndi mawu okuluwika osonyeza kuti munthu akukana ndipo sakusonyeza kuti anayankha mayi akewo mwachipongwe.
Onani Zakumapeto B14.
Kapena kuti, “msika.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “anakhulupirira dzina lake.”
Mabaibulo ena amati, “ngati sangabadwe kuchokera kumwamba.”
Kapena kuti, “zisadzudzulidwe.”
Kapena kuti, “waika chidindo chake pa umboniwo.”
Kapena kuti, “akafuna kupereka mzimu sachita kuyeza pamuyezo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Yesu.”
Kapena kuti, “pakasupepo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ola la 6,” kuwerenga kuchokera mʼma 6 koloko mʼmawa.
Kapena kuti, “mnyamata wake wachira.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “kutentha thupi.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ola la 7,” kuwerenga kuchokera mʼma 6 koloko mʼmawa.
Onani Zakumapeto A3.
Kapena kuti, “ali ndi mphatso ya moyo mwa iwo wokha.”
MʼBaibulo, “nyanja ya Galileya” imatchulidwanso ndi mayina akuti, nyanja ya Kinereti komanso nyanja ya Genesarete.
Onani Zakumapeto B14.
Mʼchilankhulo choyambirira, “Masitadiya pafupifupi 25 kapena 30.” Onani Zakumapeto B14.
Mʼchilankhulo choyambirira, “mkate wamoyo.”
Onani Zakumapeto A5.
Mʼchilankhulo choyambirira, “mulibe moyo mwa inu nokha.”
Mabaibulo ena amati, “ankaphunzitsa pamalo amene ankachitira misonkhano.”
Kapena kuti, “ndi mdyerekezi.”
Kapena kuti, “anapitiriza kuyendayenda.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “zolembedwazi anazidziwa.”
Imeneyi ndi sukulu ya Arabi.
Kapena kuti, “akamumange.”
Kapena kuti, “kumumanga.”
Mipukutu ina yakale komanso yodalirika inachotsa vesi 53 mpaka chaputala 8 vesi 11.
Kapena kuti, “potengera mfundo za anthu.”
MʼChigiriki por·nei′a. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mʼchilankhulo choyambirira, “Ndinalandira lamulo limeneli kuchokera kwa Atate wanga.”
Kapena kuti, “ndife ogwirizana.”
Kapena kuti, “ndinu ofanana ndi mulungu.”
Kapena kuti, “mʼmanda achikumbutso.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “masitadiya pafupifupi 15.” Onani Zakumapeto B14.
Kapena kuti, “kumanda achikumbutso.”
Kapena kuti, “kumanda achikumbutsowo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Sanihedirini.”
Kutanthauza kachisi.
Onani Zakumapeto B14.
Onani Zakumapeto B14.
Onani Zakumapeto A5.
Kapena kuti, “mʼmanda achikumbutso.”
Onani Zakumapeto A5.
Kapena kuti, “zimene anamva mulipoti lathu.”
Onani Zakumapeto A5.
Kapena kuti, “wandiukira.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “anakhala pachifuwa pa Yesu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Ana aangʼono inu.”
Kapena kuti, “adzakupatsani wolimbikitsa.”
Kapena kuti, “azigwirizana.”
Kapena kuti, “Apatuleni.”
Kapena kuti, “akhale ogwirizana kwambiri.”
Kapena kuti, “akanakhala kuti si chigawenga.”
Kapena kuti, “Aphedwe popachikidwa pamtengo!”
Kapena kuti, “Mutengeni mukamuphe nokha pomupachika pamtengo.”
Kapena kuti, “komanso zolamula kuti akuphe pokupachika pamtengo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ola la 6,” kuwerenga kuchokera mʼma 6 koloko mʼmawa.
Kapena kuti, “Aphedwe popachikidwa pamtengo!”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Kapena kuti, “anaweramitsa mutu nʼkutsirizika.”
Kapena kuti, “Sadzaphwanya.”
Onani Zakumapeto B14.
Kapena kuti, “manda achikumbutso.”
Kapena kuti, “kumanda achikumbutsoko.”
Kapena kuti, “pamanda achikumbutsowo.”
Kapena kuti, “mʼmanda achikumbutso.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “kukhala wosakhulupirira.”
MʼBaibulo, “nyanja ya Tiberiyo” imatchulidwanso ndi mayina akuti, nyanja ya Kinereti, nyanja ya Genesareti komanso nyanja ya Galileya.
Kapena kuti, “kodi muli ndi nsomba iliyonse.”
Kapena kuti, “chifukwa sanavale mokwanira.”
Onani Zakumapeto B14.