Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • nwt Deuteronomy 1:1-34:12
  • Deuteronomo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Deuteronomo
  • Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Deuteronomo

DEUTERONOMO

1 Awa ndi mawu amene Mose analankhula ndi Aisiraeli onse mʼchipululu, mʼchigawo cha Yorodano, mʼchigwa chimene chinali moyangʼanizana ndi Sufu, pakati pa Parana, Tofeli, Labani, Hazeroti ndi Dizahabi. 2 Kuchokera ku Horebe kupita ku Kadesi-barinea+ kudzera njira yakuphiri la Seiri pali mtunda woyenda masiku 11. 3 Mʼchaka cha 40,+ mʼmwezi wa 11, pa tsiku loyamba la mweziwo, Mose anauza Aisiraeli* zonse zimene Yehova anamuuza kuti awauze. 4 Apa nʼkuti atagonjetsa Sihoni+ mfumu ya Aamori imene inkakhala ku Hesiboni komanso Ogi+ mfumu ya Basana imene inkakhala ku Asitaroti. Mfumu imeneyi anaigonjetsera ku Edirei.+ 5 Mose anayamba kufotokoza Chilamulo+ ichi mʼchigawo cha Yorodano mʼdziko la Mowabu kuti:

6 “Yehova Mulungu wathu anatiuza tili ku Horebe kuti, ‘Mwakhalitsa mʼdera lamapiri lino.+ 7 Tembenukani mulowere kudera lamapiri la Aamori+ komanso kwa anthu onse oyandikana nawo okhala ku Araba,+ kudera lamapiri, ku Sefela, ku Negebu, mʼmbali mwa nyanja,+ mʼdziko la Akanani ndi ku Lebanoni*+ mpaka kumtsinje waukulu wa Firate.+ 8 Taonani, ndikukupatsani dzikolo. Mukalowe mʼdzikolo nʼkulitenga kuti likhale lanu, dziko limene Yehova analumbira kwa makolo anu, Abulahamu, Isaki+ ndi Yakobo,+ kuti adzalipereka kwa iwo ndi kwa mbadwa* zawo.’+

9 Pa nthawi imeneyo ndinakuuzani kuti, ‘Sindikwanitsa ndekha kugwira ntchito yokutsogolerani.+ 10 Yehova Mulungu wanu wakuchulukitsani ndipo onani, lero mwachulukadi ngati nyenyezi zakuthambo.+ 11 Yehova Mulungu wa makolo anu achulukitse chiwerengero chanu+ kuwirikiza maulendo 1,000, ndipo akudalitseni mogwirizana ndi zimene anakulonjezani.+ 12 Inuyo ndinu mtolo ndi katundu wolemera. Ndingathe bwanji kukusenzani ndekha, ndi mtima wanu wokonda mikanganowo?+ 13 Sankhani amuna anzeru, aluso ndi ozindikira mʼmafuko anu, kuti ndiwaike kukhala atsogoleri anu.’+ 14 Ndiye inu munandiuza kuti, ‘Zimene mwatiuza kuti tichitezi ndi zabwino.’ 15 Choncho ndinatenga atsogoleri a mafuko anu, amuna anzeru ndi ozindikira nʼkuwaika kukhala atsogoleri a magulu a anthu 1,000, atsogoleri a magulu a anthu 100, atsogoleri a magulu a anthu 50, atsogoleri a magulu a anthu 10 ndi akapitawo a mʼmafuko anu.+

16 Pa nthawi imeneyo ndinauza oweruza anu kuti, ‘Mukamaweruza mlandu pakati pa abale anu, muziweruza mwachilungamo+ pakati pa munthu ndi mʼbale wake kapena ndi mlendo.+ 17 Musamakondere poweruza mlandu.+ Munthu wamba ndi munthu wolemekezeka, onse muziwamvetsera chimodzimodzi.+ Musamaope anthu+ chifukwa mukuweruzira Mulungu+ ndipo ngati mlandu wakuvutani muzibwera nawo kwa ine kuti ndiumve.’+ 18 Pa nthawi imeneyo ndinakuuzani zonse zimene muyenera kuchita.

19 Kenako tinachoka ku Horebe nʼkudutsa mʼchipululu chachikulu ndi chochititsa mantha+ chonse chija chimene munachiona popita kudera lamapiri la Aamori,+ mogwirizana ndi zimene Yehova Mulungu wathu anatilamula, ndipo pamapeto pake tinafika ku Kadesi-barinea.+ 20 Ndiyeno ndinakuuzani kuti, ‘Mwafika mʼdera lamapiri la Aamori, limene Yehova Mulungu wathu akufuna kutipatsa. 21 Onani, Yehova Mulungu wanu wakupatsani dzikoli. Pitani, kalitengeni kuti likhale lanu, mogwirizana ndi zimene Yehova, Mulungu wa makolo anu anakuuzani.+ Musaope kapena kuchita mantha.’

22 Koma nonse munabwera kwa ine nʼkundiuza kuti, ‘Tiyeni titumize amuna kuti akatifufuzire zokhudza dzikolo ndipo adzatiuze njira imene tikuyenera kudzera ndiponso mizinda imene tikaipeze kumeneko.’+ 23 Ine ndinaona kuti amenewo anali maganizo abwino, moti ndinasankha amuna 12 pakati panu, mmodzi pa fuko lililonse.+ 24 Choncho iwo ananyamuka nʼkupita kudera lamapiri+ mpaka anakafika kuchigwa cha Esikolo,* ndipo anazonda dzikolo. 25 Iwo anatengako zina mwa zipatso zamʼdzikolo nʼkutibweretsera, ndipo anatiuza kuti, ‘Dziko limene Yehova Mulungu wathu akufuna kutipatsa ndi labwino.’+ 26 Koma inu munakana kupita kukalowa mʼdzikolo, ndipo munapandukira lamulo la Yehova Mulungu wanu.+ 27 Choncho munapitiriza kungʼungʼudza mʼmatenti anu kuti, ‘Yehova anatitulutsa mʼdziko la Iguputo chifukwa choti ankadana nafe, ndipo akufuna kutipereka mʼmanja mwa Aamori kuti atiwononge. 28 Kodi tikupita kuti? Abale athu achititsa mantha mitima yathu*+ potiuza kuti, “Kumeneko kuli anthu amphamvu zawo ndiponso ataliatali kuposa ifeyo ndipo mizinda yawo ndi ikuluikulu komanso ili ndi mipanda yolimba kwambiri yofika kumwamba.*+ Tinaonakonso ana a Anaki+ kumeneko.”’

29 Ndiye ine ndinakuuzani kuti, ‘Musachite mantha kapena kuwaopa.+ 30 Yehova Mulungu wanu adzakutsogolerani ndipo adzakumenyerani nkhondo,+ ngati mmene anachitira ku Iguputo inu mukuona.+ 31 Komanso munaona mʼchipululu mmene Yehova Mulungu wanu anakunyamulirani ngati mmene bambo amanyamulira mwana wake. Ankakunyamulani kulikonse kumene munkapita mpaka kudzafika pamalo ano.’ 32 Ngakhale kuti anakuchitirani zonsezi, simunakhulupirire Yehova Mulungu wanu,+ 33 amene ankayenda patsogolo panu kuti akufufuzireni malo oti mumangepo msasa. Usiku ankakutsogolerani ndi moto ndipo masana ankakutsogolerani ndi mtambo kuti akusonyezeni njira yoti muyendemo.+

34 Nthawi yonseyi Yehova ankamva zimene munkanena ndipo anakwiya kwambiri, moti analumbira kuti,+ 35 ‘Palibe munthu ndi mmodzi yemwe mwa anthu a mʼbadwo woipa uwu amene adzaone dziko labwino limene ndinalumbira kuti ndidzalipereka kwa makolo anu,+ 36 kupatulapo Kalebe mwana wa Yefune. Iyeyu adzaliona, ndipo ndidzapereka dziko limene anafikako kwa iye ndi ana ake, chifukwa chakuti watsatira Yehova ndi mtima wonse.+ 37 (Ngakhale inenso Yehova anandikwiyira chifukwa cha inu, ndipo anati, “Iwenso sukalowa mʼdziko limeneli.+ 38 Yoswa mwana wa Nuni, amene akukutumikira+ ndi amene akalowe mʼdzikomo.+ Umulimbitse,*+ chifukwa ndi amene adzatsogolere Aisiraeli pokatenga dzikolo kukhala lawo.”) 39 Komanso ana anu amene munanena kuti adzagwidwa ndi adani,+ ana anu amene lero sakudziwa chabwino kapena choipa, amenewa ndi amene adzalowe mʼdzikolo ndipo ndidzawapatsa dzikolo kuti likhale lawo.+ 40 Koma inu mubwerere, mupite kuchipululu kudzera njira yopita ku Nyanja Yofiira.’+

41 Zitatero munandiuza kuti, ‘Tachimwira Yehova. Tsopano tipita kukamenya nkhondo mogwirizana ndi zimene Yehova Mulungu wathu watilamula!’ Choncho aliyense wa inu anamanga mʼchiuno zida zake zankhondo, ndipo munkaganiza kuti zikhala zosavuta kukwera phirilo.+ 42 Koma Yehova anandiuza kuti, ‘Auze kuti: “Musapite kukamenya nkhondo, chifukwa ine sindikhala nanu.+ Mukapita, adani anu akakugonjetsani.”’ 43 Choncho ine ndinalankhula nanu, koma inu simunamvere. Mʼmalomwake, munapandukira lamulo la Yehova nʼkuchita zinthu modzikuza, moti munanyamuka kupita mʼphirimo. 44 Kenako Aamori amene ankakhala mʼphirimo anatuluka kudzakumana nanu ndipo anakuthamangitsani ngati mmene njuchi zimachitira, moti anakubalalitsani ku Seiri mpaka kukafika ku Horima. 45 Zitatero munabwerera nʼkuyamba kulira pamaso pa Yehova, koma Yehova sanakumvereni kapena kukulabadirani. 46 Nʼchifukwa chake munakhala ku Kadesi masiku ambiri.”

2 “Ndiyeno tinatembenuka nʼkulowera kuchipululu kudzera njira ya ku Nyanja Yofiira, mogwirizana ndi zimene Yehova anandiuza.+ Ndipo tinayenda masiku ambiri mʼdera lapafupi ndi phiri la Seiri. 2 Kenako Yehova anandiuza kuti, 3 ‘Mwayenda kwa nthawi yaitali mʼdera lapafupi ndi phirili. Tsopano mulowere kumpoto. 4 Auze anthuwo kuti: “Mudutsa mʼmalire a dziko la abale anu, mbadwa za Esau,+ amene akukhala ku Seiri.+ Iwo adzachita nanu mantha,+ choncho muyenera kukhala osamala kwambiri. 5 Musalimbane nawo,* chifukwa sindikupatsani mbali iliyonse ya dziko lawo, ngakhale kachigawo kokwana phazi limodzi lokha, chifukwa ndinapereka phiri la Seiri kwa Esau kuti likhale malo ake.+ 6 Mudzawapatse ndalama pa chakudya chimene mudzadye, ndipo mudzapereke ndalama pa madzi amene mudzamwe.+ 7 Chifukwa Yehova Mulungu wanu wakudalitsani pa chilichonse chimene mukuchita. Iye akudziwa bwino kuti mukuyenda mʼchipululu chachikuluchi. Yehova Mulungu wanu wakhala nanu zaka 40 zimenezi, ndipo simunasowe kanthu.”’+ 8 Choncho tinadutsa pafupi ndi abale athu, mbadwa za Esau,+ amene akukhala ku Seiri, ndipo sitinayende njira ya Araba, Elati ndi Ezioni-geberi.+

Kenako tinatembenuka nʼkudutsa njira ya mʼchipululu cha Mowabu.+ 9 Ndiyeno Yehova anandiuza kuti, ‘Usalimbane ndi Amowabu kapena kuchita nawo nkhondo, chifukwa sindidzakupatsa mbali iliyonse ya dziko lawo kuti likhale lako. Ndinapereka Ari kwa mbadwa za Loti+ kuti akhale malo awo. 10 (Kale mʼdzikoli munkakhala Aemi,+ anthu amphamvu kwambiri ndiponso ochuluka. Iwo anali ataliatali ngati Aanaki. 11 Arefai+ nawonso ankaoneka ngati Aanaki,+ ndipo Amowabu ankawatchula kuti Aemi. 12 Poyamba, Ahori+ ankakhala ku Seiri, koma mbadwa za Esau zinawalanda dzikolo nʼkuwapha ndipo iwo anayamba kukhala mʼdzikolo,+ mofanana ndi zimene Aisiraeli adzachite ndi dziko limene ndi cholowa chawo, limene Yehova adzawapatsadi.) 13 Tsopano nyamukani muwoloke chigwa cha Zeredi.’* Choncho tinawolokadi chigwa cha Zeredi.+ 14 Panadutsa zaka 38 kuti tiyende kuchokera ku Kadesi-barinea nʼkuwoloka chigwa cha Zeredi,* mpaka mʼbadwo wonse wa amuna opita kunkhondo utatha pakati pathu, mogwirizana ndi zimene Yehova analumbira kwa iwo.+ 15 Pogwiritsa ntchito dzanja lake, Yehova anawachotsa pakati panu mpaka onse anatha.+

16 Amuna onse opita kunkhondo pakati pa anthuwo atatha kufa,+ 17 Yehova analankhulanso ndi ine kuti, 18 ‘Lero mudutsa malire a dziko la Mowabu, kapena kuti Ari. 19 Mukafika pafupi ndi Aamoni, musawavutitse kapena kulimbana nawo, chifukwa sindidzakupatsani mbali iliyonse ya dziko la Aamoni kuti likhale lanu. Dziko limeneli ndinalipereka kwa mbadwa za Loti kuti likhale lawo.+ 20 Dziko limenelinso linkadziwika kuti ndi la Arefai.+ (Kale mʼdzikoli munkakhala Arefai ndipo Aamoni ankawatchula kuti Azamuzumi. 21 Anthu amenewa anali amphamvu kwambiri komanso ochuluka ndipo anali ataliatali ngati Aanaki.+ Koma Yehova anawagonjetsa pamaso pa Aamoni, ndipo Aamoniwo anawathamangitsa moti anatenga dzikolo nʼkumakhalamo. 22 Mulungu anachitanso zimenezi kwa mbadwa za Esau zimene zikukhala ku Seiri.+ Iye anagonjetsa Ahori+ pamaso pawo kuti mbadwa za Esauzo zitenge dzikolo nʼkumakhalamo mpaka lero. 23 Koma Aavi ankakhala mʼmidzi mpaka kukafika ku Gaza.+ Iwo ankakhala mʼmidzi imeneyi mpaka pamene Akafitorimu+ ochokera ku Kafitori,* anawawononga nʼkuyamba kukhala mʼmidzi yawoyo.)

24 Nyamukani ndipo muwoloke chigwa cha Arinoni.*+ Taonani, ndapereka mʼmanja mwanu Sihoni+ yemwe ndi munthu wa Chiamori, mfumu ya Hesiboni. Choncho yambani kulanda dziko lake ndipo muchite naye nkhondo. 25 Lero ndichititsa kuti anthu onse okhala pansi pa thambo, amene amva za inu, achite nanu mantha kwambiri nʼkuyamba kukuopani. Iwo adzasokonezeka maganizo ndipo adzanjenjemera* chifukwa cha inu.’+

26 Kenako ndinatumiza amithenga kuchokera mʼchipululu cha Kademoti+ kupita kwa Mfumu Sihoni ya ku Hesiboni, kuti akanene uthenga wamtendere kuti,+ 27 ‘Ndilole ndidutse mʼdziko lako. Ndidzangodutsa mumsewu ndipo sindidzakhotera kudzanja lamanja kapena lamanzere.+ 28 Ndidzadya chakudya komanso kumwa madzi amene udzandigulitse. Ungondilola kuti ndidutse mʼdziko lako 29 mpaka kukawoloka Yorodano nʼkulowa mʼdziko limene Yehova Mulungu wathu anatipatsa. Izi nʼzimene mbadwa za Esau zimene zikukhala ku Seiri komanso Amowabu amene akukhala ku Ari anandichitira.’ 30 Koma Mfumu Sihoni ya ku Hesiboni sinatilole kuti tidutse mʼdziko lake, chifukwa Yehova Mulungu wanu anamulola kuti akhale wokanika+ komanso kuti aumitse mtima wake, nʼcholinga choti amupereke mʼmanja mwanu monga mmene zilili lero.+

31 Kenako Yehova anandiuza kuti, ‘Taona, ndayamba kale kupereka Sihoni ndi dziko lake kwa iwe. Yamba kulanda dziko lake.’+ 32 Sihoni atatuluka pamodzi ndi anthu ake onse kudzamenya nafe nkhondo ku Yahazi,+ 33 Yehova Mulungu wathu anamupereka kwa ife ndipo tinamugonjetsa limodzi ndi ana ake komanso anthu ake onse. 34 Pa nthawi imeneyo, tinalanda mizinda yake yonse ndi kuwononga mzinda wina uliwonse. Tinapha amuna, akazi ndi ana ndipo sitinasiye munthu aliyense ndi moyo.+ 35 Ziweto zokha nʼzimene tinatenga pamodzi ndi zinthu zimene tinatenga mʼmizinda imene tinalanda. 36 Kuchokera ku Aroweli,+ mzinda umene uli mʼmbali mwa chigwa cha Arinoni,* (kuphatikizapo mzinda umene uli mʼchigwacho), mpaka kukafika ku Giliyadi, panalibe mzinda umene sitinathe kuugonjetsa. Yehova Mulungu wathu anawapereka onsewo kwa ife.+ 37 Koma simunayandikire dziko la Aamoni,+ dera lonse lamʼmbali mwa chigwa cha Yaboki,*+ kapena mizinda yamʼdera lamapiri, kapenanso malo alionse amene Yehova Mulungu wathu anatiletsa.”

3 “Ndiyeno tinatembenuka nʼkulowera Njira ya ku Basana. Ndipo Ogi mfumu ya ku Basana anabwera limodzi ndi anthu ake onse kudzamenyana nafe ku Edirei.+ 2 Ndiyeno Yehova anandiuza kuti, ‘Usamuope ameneyu, chifukwa ndipereka iyeyo pamodzi ndi anthu ake onse komanso dziko lake mʼmanja mwako. Umuchite zimene unachitira Sihoni mfumu ya Aamori, amene ankakhala ku Hesiboni.’ 3 Choncho Yehova Mulungu wathu anaperekanso Ogi mfumu ya Basana ndi anthu ake onse mʼmanja mwathu, ndipo tinawapha moti panalibe munthu ngakhale mmodzi mwa anthu ake, yemwe anapulumuka. 4 Kenako tinalanda mizinda yake yonse. Panalibe mzinda umene sitinaulande. Tinalanda mizinda 60 mʼchigawo chonse cha Arigobi, mʼdera lonse la ufumu wa Ogi ku Basana.+ 5 Mizinda yonseyi inali yamipanda yolimba yomwe inali ndi makoma aatali, zitseko ndiponso mipiringidzo. Tinalandanso matauni ambirimbiri akumidzi. 6 Koma mizinda yonseyo tinaiwononga+ ngati mmene tinachitira ndi Mfumu Sihoni ya ku Hesiboni, tinawononga mzinda uliwonse kuphatikizapo amuna, akazi ndi ana.+ 7 Ndipo tinatenga ziweto ndi zinthu zonse zamʼmizindayo.

8 Pa nthawi imeneyo tinalanda dziko la mafumu awiri a Aamori+ amene ankakhala mʼdera la Yorodano, kuyambira mʼchigwa cha Arinoni* mpaka kuphiri la Herimoni.+ 9 (Phiri limeneli Asidoni ankalitchula kuti Sirioni, pamene Aamori ankalitchula kuti Seniri.) 10 Tinalanda mizinda yonse yakudera lokwererapo, mʼGiliyadi monse, mʼBasana monse, mpaka ku Saleka ndi ku Edirei,+ mizinda imene inali mu ufumu wa Ogi ku Basana. 11 Ogi mfumu ya ku Basana ndi amene anali womaliza pa Arefai amene anatsala. Chithatha chimene* anaikapo mtembo wake chinali chachitsulo ndipo mpaka pano chidakali ku Raba wa Aamoni. Mulitali mwake nʼchokwana masentimita 401,* ndipo mulifupi mwake masentimita 178,* potengera muyezo umene unakhazikitsidwa. 12 Pa nthawi imeneyo tinatenga dzikoli kukhala lathu kuchokera ku Aroweli,+ mzinda umene uli mʼchigwa cha Arinoni* ndi hafu ya dera lamapiri la Giliyadi. Ndipo ndinapereka mizinda yake kwa fuko la Rubeni ndi fuko la Gadi.+ 13 Mbali yotsala ya dera la Giliyadi ndi Basana yense amene anali mu ufumu wa Ogi ndinaipereka kwa hafu ya fuko la Manase.+ Dera lonse la Arigobi, limene ndi mbali ya Basana linkadziwika kuti ndi dziko la Arefai.

14 Yairi+ mwana wamwamuna wa Manase anatenga dera lonse la Arigobi+ mpaka kumalire a Agesuri ndi a Amaakati.+ Midzi ya ku Basana imeneyo anaipatsa dzina lofanana ndi lake lakuti, Havoti-yairi*+ ndipo imadziwika ndi dzina limeneli mpaka pano. 15 Makiri ndinamupatsa dera la Giliyadi.+ 16 Mafuko a Rubeni ndi Gadi+ ndinawapatsa dera lochokera ku Giliyadi kukafika kuchigwa cha Arinoni,* ndipo malire anali pakati pa chigwacho. Dera limeneli linakafikanso kuchigwa cha Yaboki, amene ndi malire a Aamoni. 17 Ndinawapatsanso Araba, mtsinje wa Yorodano ndi malo amʼmbali mwa mtsinjewo, kuchokera ku Kinereti* mpaka kunyanja ya Araba. Imeneyi ndi Nyanja Yamchere* imene ili mʼmunsi mwa zitunda za Pisiga, chakumʼmawa.+

18 Pa nthawi imeneyo ndinakulamulani kuti: ‘Yehova Mulungu wanu wakupatsani dzikoli kuti mulitenge kukhala lanu. Amuna onse olimba mtima atenge zida ndipo awoloke patsogolo pa abale anu, Aisiraeli.+ 19 Akazi anu okha ndi ana anu ndi amene atsale mʼmizinda imene ndakupatsani. Ziweto zanunso zitsale (ndikudziwa kuti muli ndi ziweto zambiri), 20 mpaka Yehova atapereka mpumulo kwa abale anu, ngati mmene wachitira ndi inu ndiponso mpaka iwo atatenga dziko limene Yehova Mulungu wanu akuwapatsa tsidya linalo la Yorodano. Mukatero mudzabwerera, aliyense kumalo ake amene ndakupatsani.’+

21 Pa nthawi imeneyo ndinalamula Yoswa+ kuti: ‘Iwe waona ndi maso ako zonse zimene Yehova Mulungu wanu wachitira mafumu awiriwa. Yehova adzachitanso chimodzimodzi ndi maufumu onse amene ali kumene mukuwolokera kukamenyana nawo.+ 22 Musawaope amenewo, chifukwa Yehova Mulungu wanu ndi amene akukumenyerani nkhondo.’+

23 Pa nthawi imeneyo ndinachonderera Yehova kuti, 24 ‘Yehova Ambuye Wamkulu Koposa, mwayamba kuonetsa mtumiki wanu ukulu wanu ndi dzanja lanu lamphamvu.+ Ndi mulungu winanso uti, kumwamba kapena padziko lapansi, amene amachita ntchito zamphamvu ngati inu?+ 25 Ndiloleni chonde ndiwoloke, kuti ndione dziko labwino limene lili kutsidya kwa Yorodano, dera lamapiri labwinoli komanso Lebanoni.’+ 26 Koma Yehova anapitiriza kundikwiyira chifukwa cha inu,+ ndipo sanandimvere. Mʼmalomwake Yehova anandiuza kuti, ‘Basi khala chete! Usadzandiuzenso nkhani imeneyi. 27 Kwera pamwamba pa Pisiga+ ndipo ukayangʼane kumadzulo, kumpoto, kumʼmwera ndi kumʼmawa kuti ukaone dzikolo ndi maso ako, chifukwa suwoloka Yorodano uyu.+ 28 Uike Yoswa+ kuti akhale mtsogoleri ndipo umulimbikitse ndi kumulimbitsa mtima chifukwa ndi amene adzawolotse+ anthuwa ndi kuwachititsa kulandira dziko limene ulionelo kukhala cholowa chawo.’ 29 Zonsezi zinachitika tili mʼchigwa moyangʼanizana ndi Beti-peori.”+

4 “Tsopano inu Aisiraeli, mverani malangizo ndi zigamulo zimene ndikukuphunzitsani kuti muzitsatira. Mukatero mudzakhala ndi moyo+ nʼkukalowa mʼdziko limene Yehova Mulungu wa makolo anu akukupatsani kuti mukalitenge nʼkukhala lanu. 2 Musawonjezerepo kalikonse pa mawu amene ndikukulamulani, ndipo musachotsepo kalikonse pa mawu amenewa,+ kuti muzisunga malamulo a Yehova Mulungu wanu amene ndikukupatsani.

3 Inu munaona ndi maso anu zimene Yehova anachita pa nkhani ya Baala wa ku Peori. Yehova Mulungu wanu anawononga pakati panu munthu aliyense amene anatsatira Baala wa ku Peori.+ 4 Koma nonsenu amene mwagwiritsitsa Yehova Mulungu wanu muli ndi moyo lero. 5 Taonani, ndakuuzani malangizo ndi zigamulo,+ mogwirizana ndi zimene Yehova Mulungu wanga wandilamula, kuti muzikatsatira zimenezo mʼdziko limene mukupita kukalitenga kuti likhale lanu. 6 Muzitsatira malangizo ndi zigamulo zimenezi mosamala kwambiri,+ chifukwa mukachita zimenezi mudzasonyeza kuti ndinu anzeru+ komanso ozindikira+ pamaso pa anthu a mitundu ina amene adzamva za malangizo onsewa ndipo adzanena kuti, ‘Mtundu waukulu umenewu ndi wa anthu anzerudi komanso ozindikira.’+ 7 Pajatu Yehova Mulungu wathu amayankha mapemphero athu nthawi zonse. Kodi pali mtundu winanso wamphamvu umene milungu yake ili nawo pafupi chonchi?+ 8 Ndipo ndi mtundu winanso uti wamphamvu umene uli ndi malangizo komanso zigamulo zolungama zofanana ndi Chilamulo chonsechi chimene ndikukupatsani lero?+

9 Koma samalani ndipo mukhale tcheru* kuti musaiwale zinthu zimene maso anu anaona, komanso kuti zinthu zimenezo zisachoke mumtima mwanu masiku onse a moyo wanu. Ana anu ndi zidzukulu zanu muziwauzanso zinthu zimenezo.+ 10 Pa tsiku limene munaima pamaso pa Yehova Mulungu wanu ku Horebe, Yehova anandiuza kuti, ‘Sonkhanitsa anthu kwa ine kuti amve mawu anga,+ nʼcholinga choti aphunzire kundiopa+ masiku onse amene iwo adzakhale ndi moyo padzikoli komanso kuti aphunzitse ana awo.’+

11 Choncho anthu inu munayandikira nʼkuimirira mʼmunsi mwa phiri. Phirilo linkayaka moto umene unkafika kumwamba,* ndipo kunali mdima ndi mtambo wakuda.+ 12 Ndiyeno Yehova anayamba kukulankhulani kuchokera mʼmoto.+ Inu munamva mawu koma simunaone kalikonse.+ Munangomva mawu okha basi.+ 13 Iye anakuuzani pangano lake,+ kapena kuti Malamulo Khumi,*+ amene anakulamulani kuti muziwatsatira. Kenako analemba Malamulowo pamiyala iwiri yosema.+ 14 Pa nthawi imeneyo Yehova anandilamula kuti ndikuphunzitseni malangizo ndi zigamulo, zimene mukuyenera kukazitsatira mukakalowa mʼdziko limene mukukalitenga kuti likhale lanu.

15 Mukhale tcheru,* chifukwa pa tsiku limene Yehova analankhula nanu kuchokera pakati pa moto ku Horebe, simunaone kalikonse mʼmotowo. 16 Choncho musamale kuti musachite zinthu mosakhulupirika popanga chifaniziro chilichonse chosema, chifaniziro cha chinthu chilichonse chachimuna kapena chachikazi,+ 17 chifaniziro cha nyama iliyonse yapadziko lapansi kapena chifaniziro cha mbalame iliyonse youluka mumlengalenga,+ 18 chifaniziro cha chinthu chilichonse chimene chimakwawa panthaka kapena chifaniziro cha nsomba iliyonse yamʼmadzi apansi pa dziko.+ 19 Mukakweza maso anu kuthambo nʼkuona dzuwa, mwezi ndi nyenyezi, gulu lonse la zinthu zakuthambo, musakopeke nazo nʼkuyamba kuzigwadira komanso kuzitumikira.+ Yehova Mulungu wanu wazipereka kwa anthu onse okhala pansi pa thambo lonse. 20 Musachite zimenezo chifukwa Yehova ndi amene anakutengani nʼkukutulutsani mungʼanjo yosungunulira zitsulo, anakutulutsani mu Iguputo, kuti mukhale anthu ake,*+ monga mmene mulili lero.

21 Yehova anandikwiyira chifukwa cha inu,+ ndipo analumbira kuti sadzandilola kuti ndiwoloke Yorodano kapena kupita mʼdziko labwino limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani kuti likhale cholowa chanu.+ 22 Ineyo ndifera mʼdziko lino. Sindiwoloka Yorodano,+ koma inu muwoloka nʼkukatenga dziko labwinoli. 23 Samalani kuti musaiwale pangano la Yehova Mulungu wanu limene anachita ndi inu+ ndipo musapange chifaniziro chosema, chifaniziro cha chinthu chilichonse chimene Yehova Mulungu wanu anakuletsani.+ 24 Chifukwa Yehova Mulungu wanu ndi moto wowononga,+ iye ndi Mulungu amene amafuna kuti anthu azidzipereka kwa iye yekha basi.+

25 Mukakakhala ndi ana komanso zidzukulu ndipo mukakakhala nthawi yaitali mʼdzikomo, nʼkuchita zinthu zokuwonongetsani popanga chifaniziro chosema+ cha chinthu chilichonse, nʼkuchita choipa pamaso pa Yehova Mulungu wanu, moti nʼkumukhumudwitsa,+ 26 ndikutenga kumwamba ndi dziko lapansi lero monga mboni zokutsutsani, kuti mudzafa mwamsanga mʼdziko limene mukupita kukalitenga mutawoloka Yorodano. Simudzakhala mʼdzikomo kwa nthawi yaitali chifukwa mudzawonongedwa ndithu.+ 27 Yehova adzakubalalitsani pakati pa anthu a mitundu ina,+ ndipo anthu ochepa okha pakati panu ndi amene adzapulumuke+ mʼmayiko a mitundu imene Yehova adzakuthamangitsireni. 28 Kumeneko mudzatumikira milungu yamtengo ndi mwala, yopangidwa ndi manja a anthu,+ milungu imene singaone, kumva, kudya kapena kununkhiza.

29 Mukadzafufuza Yehova Mulungu wanu muli kumeneko, mukadzamufunafuna ndi mtima wanu wonse komanso moyo wanu wonse, mudzamupezadi.+ 30 Pamapeto pake, zinthu zonsezi zikadzakuchitikirani nʼkukhala pamavuto aakulu, mudzabwerera kwa Yehova Mulungu wanu ndipo mudzamvera mawu ake.+ 31 Pajatu Yehova Mulungu wanu ndi Mulungu wachifundo.+ Sadzakusiyani kapena kukuwonongani kapenanso kuiwala pangano limene analumbira kwa makolo anu.+

32 Tafunsani tsopano, za masiku akale inu musanakhalepo, kuchokera pa tsiku limene Mulungu analenga munthu padziko lapansi. Mufufuze kuchokera kumalekezero a thambo kukafika kumalekezero ena a thambo. Kodi zinthu zazikulu ngati zimenezi zinayamba zachitikapo, kapena kodi pali amene anamvapo zinthu ngati zimenezi?+ 33 Kodi pali anthu enanso amene anamvapo mawu a Mulungu akumveka kuchokera pamoto ngati mmene inuyo munawamvera nʼkukhalabe ndi moyo?+ 34 Kapena kodi Mulungu anayamba wapitapo kukatenga mtundu wa anthu kuti ukhale wake kuchokera pakati pa mtundu wina pogwiritsa ntchito ziweruzo,* zizindikiro, zodabwitsa,+ nkhondo,+ dzanja lamphamvu,+ mkono wotambasula komanso zinthu zoopsa+ zofanana ndi zimene Yehova Mulungu wanu anakuchitirani ku Iguputo inu mukuona? 35 Inuyo mwasonyezedwa zinthu zimenezi kuti mudziwe kuti Yehova ndi Mulungu woona.+ Palibenso Mulungu wina kupatulapo iyeyo.+ 36 Anakuchititsani kuti mumve mawu ake kuchokera kumwamba nʼcholinga chakuti akulangizeni kuti muzimumvera. Padziko lapansi pano, iye anakuchititsani kuti muone moto waukulu, ndipo munamva mawu ake kuchokera pamotowo.+

37 Chifukwa choti ankakonda makolo anu ndipo anasankha mbadwa* zawo zobwera pambuyo pawo,+ anakutulutsani ku Iguputo ndi mphamvu zake zazikulu ndipo ankakuyangʼanirani. 38 Anachotsa pamaso panu mitundu yaikulu ndi yamphamvu kuposa inu, kuti akulowetseni mʼdziko lawo nʼkukupatsani kuti likhale cholowa chanu ngati mmene zilili lero.+ 39 Choncho mudziwe lero, ndipo muzikumbukira mumtima mwanu kuti Yehova ndi Mulungu woona, kumwamba ndiponso padziko lapansi.+ Palibenso wina.+ 40 Muzisunga malangizo ndi malamulo ake amene ndikukulamulani lero kuti zikuyendereni bwino, inuyo ndi ana anu obwera pambuyo panu, kuti mukhale kwa nthawi yaitali mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani.”+

41 Pa nthawi imeneyo, Mose anapatula mizinda itatu mbali yakumʼmawa kwa Yorodano.+ 42 Ngati munthu wapha mnzake mwangozi ndipo sanayambe wadanapo naye,+ munthu ameneyu azithawira ku umodzi mwa mizinda imeneyi kuti akhale ndi moyo.+ 43 Mizinda yake ndi Bezeri,+ mʼchipululu chimene chili mʼdera lokwererapo, woti anthu a fuko la Rubeni azithawirako. Mzinda wa Ramoti+ ku Giliyadi, woti anthu a fuko la Gadi azithawirako ndi mzinda wa Golani+ ku Basana, woti anthu a fuko la Manase+ azithawirako.

44 Tsopano Chilamulo+ chimene Mose anaika pamaso pa Aisiraeli ndi ichi. 45 Chilamulocho ndi zikumbutso, malangizo ndi zigamulo zimene Mose anapatsa Aisiraeli atatuluka mu Iguputo.+ 46 Anawapatsa zimenezi ali pafupi ndi Yorodano, mʼchigwa, moyangʼanizana ndi Beti-peori.+ Dera limeneli ndi dziko la Mfumu Sihoni ya Aamori, imene inkakhala ku Hesiboni+ ndipo Mose ndi Aisiraeli anaigonjetsa atatuluka mu Iguputo.+ 47 Iwo anamulanda dziko lakelo komanso dziko la Ogi+ mfumu ya Basana. Amenewa ndi mafumu awiri a Aamori amene anali kuchigawo chakumʼmawa kwa Yorodano. 48 Dera limeneli linayambira ku Aroweli+ mʼmphepete mwa chigwa cha Arinoni* mpaka kuphiri la Sione, limene ndi phiri la Herimoni,+ 49 ndiponso dera lonse la Araba mʼchigawo chakumʼmawa kwa Yorodano, mpaka ku Nyanja ya Araba,* mʼmunsi mwa zitunda za Pisiga.+

5 Ndiyeno Mose anaitana Aisiraeli onse nʼkuwauza kuti: “Inu Aisiraeli, mverani malangizo ndi zigamulo zimene ndikukuuzani lero, ndipo muziphunzire ndi kuzitsatira mosamala. 2 Yehova Mulungu wathu anachita nafe pangano ku Horebe.+ 3 Yehova sanachite pangano limeneli ndi makolo athu, koma ndi ife, tonse amene tili pano lero. 4 Yehova analankhula nanu pamasomʼpamaso mʼphiri, kuchokera mʼmoto.+ 5 Ine ndinaima pakati pa Yehova ndi inu pa nthawi imeneyo,+ kuti ndikuuzeni mawu a Yehova. Inuyo simunakwere mʼphirimo chifukwa munkaopa moto.+ Ndiyeno Mulungu anati:

6 ‘Ine ndine Yehova Mulungu wanu, amene ndinakutulutsani mʼdziko la Iguputo, mʼnyumba yaukapolo.+ 7 Musakhale ndi milungu ina iliyonse kupatulapo ine.*+

8 Musadzipangire fano kapena chifaniziro+ cha chinthu chilichonse chakumwamba, kapena chapadziko lapansi, kapenanso chamʼmadzi apadziko lapansi. 9 Musaziweramire kapena kuzitumikira,+ chifukwa ine Yehova Mulungu wanu, ndine Mulungu amene ndimafuna kuti anthu azidzipereka kwa ine ndekha,+ amene ndimalanga ana, zidzukulu ndi ana a zidzukuluzo chifukwa cha zolakwa za abambo a anthu odana ndi ine.+ 10 Koma ndimasonyeza chikondi chokhulupirika* kwa anthu mibadwo masauzande amene amandikonda komanso kusunga malamulo anga.

11 Musagwiritse ntchito dzina la Yehova Mulungu wanu molakwika,+ chifukwa Yehova sadzalekerera aliyense wogwiritsa ntchito dzina lake molakwika osamulanga.+

12 Muzisunga tsiku la Sabata ndipo muziliona kuti ndi lopatulika, mogwirizana ndi zimene Yehova Mulungu wanu anakulamulani.+ 13 Muzigwira ntchito zanu zonse masiku 6,+ 14 koma tsiku la 7 ndi sabata la Yehova Mulungu wanu.+ Musamagwire ntchito iliyonse,+ inuyo kapena mwana wanu wamwamuna, mwana wanu wamkazi, kapolo wanu wamwamuna, kapolo wanu wamkazi, ngʼombe yanu yamphongo, bulu wanu, chiweto chanu chilichonse, kapena mlendo amene akukhala mumzinda wanu,+ kuti nayenso kapolo wanu wamwamuna ndi kapolo wanu wamkazi, azipuma mofanana ndi inu.+ 15 Muzikumbukira kuti munali akapolo mʼdziko la Iguputo ndipo Yehova Mulungu wanu anakutulutsani kumeneko ndi dzanja lamphamvu komanso mkono wotambasula.+ Nʼchifukwa chake Yehova Mulungu wanu anakulamulani kuti muzisunga tsiku la Sabata.

16 Muzilemekeza bambo anu ndi mayi anu+ mogwirizana ndi zimene Yehova Mulungu wanu anakulamulani, kuti mukhale ndi moyo nthawi yaitali komanso kuti zinthu zikuyendereni bwino mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani.+

17 Musaphe munthu.*+

18 Musachite chigololo.+

19 Musabe.+

20 Musapereke umboni wonamizira mnzanu.+

21 Musalakelake mkazi wa mnzanu.+ Musalakelake mwadyera nyumba ya mnzanu, munda wake, kapolo wake wamwamuna, kapolo wake wamkazi, ngʼombe yake yamphongo, bulu wake, kapena chinthu chilichonse cha mnzanu.’+

22 Yehova anapereka malamulo* amenewa ku mpingo wanu wonse, mʼphiri. Analankhula mokweza kuchokera mʼmoto ndi mumtambo wakuda+ ndipo pa malamulowo sanawonjezerepo kalikonse. Kenako anawalemba pamiyala iwiri yosema nʼkundipatsa.+

23 Ndiyeno mutangomva mawu amenewo kuchokera pamalo amdima, phiri likuyaka moto,+ atsogoleri onse a mafuko anu ndi akulu onse anabwera kwa ine. 24 Ndiyeno munati, ‘Yehova Mulungu wathu watisonyeza ulemerero wake ndi ukulu wake, ndipo tamva mawu ake kuchokera mʼmoto.+ Lero taona kuti Mulungu angalankhule ndi munthu, munthuyo nʼkukhalabe ndi moyo.+ 25 Koma ife sitikufuna kufa, chifukwa moto waukuluwu ukhoza kutipsereza. Tikapitiriza kumvetsera mawu a Yehova Mulungu wathu ndithu tifa. 26 Kodi pali munthu aliyense amene anamvapo mawu a Mulungu wamoyo, akulankhula kuchokera mʼmoto ngati mmene ife tachitiramu nʼkukhalabe ndi moyo? 27 Iweyo upite pafupi ukamvetsere zonse zimene Yehova Mulungu wathu akanene. Ndiyeno iweyo udzatiuze zonse zimene Yehova Mulungu wathu wakuuza, ndipo ife tidzamvera nʼkuchita zomwezo.’+

28 Choncho Yehova anamva zonse zimene munandiuza, ndipo Yehova anandiuza kuti, ‘Ndamva mawu amene anthu awa akuuza. Zonse zimene anena ndi zabwino.+ 29 Zikanakhala bwino kwambiri akanakhala ndi mtima wondiopa+ ndi kusunga malamulo anga+ nthawi zonse. Akanachita zimenezi zinthu zikanawayendera bwino, iwowo ndi ana awo mpaka kalekale!+ 30 Pita ukawauze kuti: “Bwererani kumatenti anu.” 31 Koma iwe ukhale pompano, ndipo ndikuuza malamulo onse, malangizo ndi zigamulo zimene ukuyenera kuwaphunzitsa kuti azikazitsatira mʼdziko limene ndikuwapatsa kuti likhale lawo.’ 32 Ndipo anthu inu muonetsetse kuti mukuchita zimene Yehova Mulungu wanu wakulamulani.+ Musatembenukire kudzanja lamanja kapena lamanzere.+ 33 Muziyenda mʼnjira imene Yehova Mulungu wanu wakulamulani,+ kuti mukhale ndi moyo, kuti zinthu zikuyendereni bwino komanso kuti mukhale ndi moyo wautali mʼdziko limene mudzalitenge kuti likhale lanu.”+

6 “Tsopano amenewa ndi malamulo, malangizo ndi zigamulo zimene Yehova Mulungu wanu wandipatsa kuti ndikuphunzitseni, kuti muzikazitsatira mukawoloka mtsinje wa Yorodano nʼkupita mʼdziko limene mukukalitenga kuti likhale lanu, 2 kuti muziopa Yehova Mulungu wanu ndi kutsatira malangizo ake komanso malamulo ake amene ndikukuuzani, inuyo, ana anu ndi zidzukulu zanu,+ masiku onse a moyo wanu, nʼcholinga choti mukhale ndi moyo nthawi yaitali.+ 3 Ndipo inu Aisiraeli, muzimvetsera ndi kutsatira malangizo ndi malamulo akewo mosamala, kuti zinthu zikuyendereni bwino komanso kuti muchuluke kwambiri mʼdziko loyenda mkaka ndi uchi, mogwirizana ndi zimene Yehova, Mulungu wa makolo anu anakulonjezani.

4 Tamverani, Aisiraeli inu: Yehova Mulungu wathu ndi Yehova mmodzi.+ 5 Muzikonda Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, moyo wanu wonse+ ndi mphamvu zanu zonse.+ 6 Mawu awa amene ndikukulamulani lerowa azikhala pamtima panu, 7 ndipo muziwakhomereza* mumtima mwa ana anu.+ Muzilankhula nawo mawuwo mukakhala pansi mʼnyumba mwanu, mukamayenda pamsewu, mukamagona komanso mukadzuka.+ 8 Muwamange padzanja lanu kuti muziwakumbukira, ndipo azikhala ngati chomanga pachipumi panu.*+ 9 Muwalembe pamafelemu a nyumba zanu komanso pamageti a mzinda wanu.

10 Ndiyeno Yehova Mulungu wanu akadzakulowetsani mʼdziko limene analumbira kwa makolo anu Abulahamu, Isaki ndi Yakobo kuti adzakupatsani,+ dziko lokhala ndi mizinda ikuluikulu yabwino imene simunamange ndinu,+ 11 yokhalanso ndi nyumba zodzaza ndi zinthu zosiyanasiyana zabwino zimene simunagwirire ntchito, zitsime zimene simunakumbe ndinu komanso minda ya mpesa ndi mitengo ya maolivi imene simunadzale ndinu, ndiye mukakadya nʼkukhuta,+ 12 mukasamale kuti musakaiwale Yehova+ amene anakutulutsani mʼdziko la Iguputo, mʼnyumba yaukapolo. 13 Muziopa Yehova Mulungu wanu+ nʼkumamutumikira,+ ndipo muzilumbira pa dzina lake.+ 14 Musatsatire milungu ina, milungu iliyonse ya anthu amene akuzungulirani,+ 15 chifukwa Yehova Mulungu wanu amene ali pakati panu ndi Mulungu amene amafuna kuti anthu azidzipereka kwa iye yekha basi.+ Mukatsatira milungu ina, mkwiyo wa Yehova Mulungu wanu udzakuyakirani+ ndipo adzakufafanizani padziko lapansi.+

16 Yehova Mulungu wanu musamamuyese+ ngati mmene munamuyesera ku Masa.+ 17 Muzionetsetsa kuti mukusunga malamulo a Yehova Mulungu wanu, zikumbutso zake ndi malangizo ake amene wakulamulani kuti muziwatsatira. 18 Muzichita zoyenera ndi zabwino pamaso pa Yehova kuti zikuyendereni bwino komanso kuti mukalowe mʼdziko labwino limene Yehova analumbira kwa makolo anu, nʼkulitenga kuti likhale lanu,+ 19 pothamangitsa adani anu onse mogwirizana ndi zimene Yehova analonjeza.+

20 Mʼtsogolo mwana wanu akadzakufunsani kuti, ‘Kodi zikumbutso, malangizo ndi zigamulo zimene Yehova Mulungu wathu anakupatsani zimatanthauza chiyani?’ 21 mwana wanuyo mudzamuyankhe kuti, ‘Tinali akapolo a Farao ku Iguputo, koma Yehova anatitulutsa ku Iguputoko ndi dzanja lamphamvu. 22 Choncho Yehova anapitiriza kuchita zizindikiro ndi zodabwitsa zazikulu ndiponso zowononga mu Iguputo monse,+ kwa Farao ndi kwa anthu onse amʼnyumba mwake, ife tikuona.+ 23 Ndipo anatitulutsa kumeneko kuti atibweretse kuno kudzatipatsa dziko limene analumbira kwa makolo athu.+ 24 Ndiyeno Yehova anatilamula kuti tizitsatira malangizo onsewa komanso kuti tiziopa Yehova Mulungu wathu kuti zinthu zizitiyendera bwino nthawi zonse,+ komanso kuti tikhale ndi moyo+ ngati mmene zilili lero. 25 Ndipo tikamatsatira malamulo onsewa mosamala kwambiri pomvera* Yehova Mulungu wathu mogwirizana ndi zimene anatilamula, ndiye kuti tikuchita chilungamo pamaso pake.’”+

7 “Yehova Mulungu wanu akadzakulowetsani mʼdziko limene mwatsala pangʼono kulitenga kuti likhale lanu,+ adzakuchotseraninso mitundu ikuluikulu.+ Adzakuchotserani Ahiti, Agirigasi, Aamori,+ Akanani, Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi,+ mitundu 7 ikuluikulu komanso yamphamvu kuposa inu.+ 2 Yehova Mulungu wanu adzawapereka kwa inu ndipo mudzawagonjetsa.+ Mudzawawononge+ ndithu ndipo musadzachite nawo pangano lililonse kapena kuwakomera mtima.+ 3 Musadzachite nawo mgwirizano uliwonse wa ukwati.* Musadzapereke ana anu aakazi kwa ana awo aamuna ndipo musadzatenge ana awo aakazi nʼkuwapereka kwa ana anu aamuna.+ 4 Chifukwa adzachititsa kuti ana anu aamuna asiye kunditsatira ndipo adzatumikira milungu ina.+ Ndiyeno mkwiyo wa Yehova udzakuyakirani ndipo adzakuwonongani mofulumira.+

5 Koma inu mudzawachitire zotsatirazi: Mudzagwetse maguwa awo ansembe komanso kuphwanya zipilala zawo zopatulika.+ Mudzadule mizati yawo yopatulika+ ndi kuwotcha zifaniziro zawo zogoba.+ 6 Chifukwa ndinu anthu oyera kwa Yehova Mulungu wanu. Yehova Mulungu wanu anakusankhani kuti mukhale anthu ake, chuma chake chapadera, pa anthu onse okhala padziko lapansi.+

7 Sikuti Yehova anakusonyezani chikondi ndi kukusankhani+ chifukwa chakuti munali ochuluka kuposa mitundu yonse, chifukwatu mtundu wanu unali waungʼono mwa mitundu yonse.+ 8 Koma Yehova anakutulutsani ndi dzanja lamphamvu kuti akulanditseni mʼnyumba yaukapolo,+ mʼmanja mwa Farao* mfumu ya Iguputo, chifukwa chakuti Yehova anakukondani, komanso chifukwa chosunga lumbiro lake limene analumbirira makolo anu.+ 9 Inu mukudziwa bwino kuti Yehova Mulungu wanu ndi Mulungu woona, Mulungu wokhulupirika, amene amasunga pangano lake ndiponso amasonyeza chikondi chokhulupirika kwa anthu amene amamukonda ndi kusunga malamulo ake ku mibadwo 1,000.+ 10 Koma anthu amene amadana naye adzawabwezera powawononga.+ Iye sadzazengereza kupereka chilango kwa anthu amene amadana naye koma adzawabwezera powawononga. 11 Choncho muzionetsetsa kuti mukusunga malamulo, malangizo ndi zigamulo zimene ndikukupatsani lero, pozitsatira.

12 Ngati mutapitiriza kumvera zigamulo zimenezi ndi kuzitsatira, Yehova Mulungu wanu adzasunga pangano ndi kukusonyezani chikondi chokhulupirika, zimene analumbira kwa makolo anu. 13 Iye adzakukondani, kukudalitsani komanso kukuchulukitsani. Adzakudalitsani ndithu pokupatsani ana ambiri,*+ adzadalitsa zokolola za nthaka yanu, mbewu zanu, vinyo wanu watsopano, mafuta anu,+ ana a ngʼombe zanu ndi ana a nkhosa zanu, mʼdziko limene analumbira kwa makolo anu kuti adzakupatsani.+ 14 Inu mudzakhala odalitsika kwambiri mwa anthu onse.+ Pakati panu sipadzapezeka mwamuna, mkazi kapena chiweto chosabereka.+ 15 Yehova adzakuchotserani matenda onse ndipo sadzakugwetserani matenda alionse oopsa amene munawaona ku Iguputo.+ Koma adzawagwetsera pa anthu onse amene amadana nanu. 16 Muwononge anthu a mitundu yonse amene Yehova Mulungu wanu akuwapereka kwa inu.+ Musawamvere chisoni+ ndipo musatumikire milungu yawo+ chifukwa kuchita zimenezo kudzakutcherani msampha.+

17 Mukaganiza mumtima mwanu kuti, ‘Anthu a mitundu iyi ndi ambiri kuposa ife. Tingathe bwanji kuwathamangitsa?’+ 18 musawaope.+ Nthawi zonse muzikumbukira zimene Yehova Mulungu wanu anachitira Farao ndi Iguputo yense.+ 19 Muzikumbukira ziweruzo zamphamvu zimene* maso anu anaona, zizindikiro, zodabwitsa,+ dzanja lamphamvu ndiponso mkono wotambasula umene Yehova Mulungu wanu anagwiritsa ntchito pokutulutsani mʼdzikolo.+ Izi ndi zimene Yehova Mulungu wanu adzachite ndi anthu a mitundu yonse amene mukuwaopa.+ 20 Yehova Mulungu wanu adzachititsa mantha mitima yawo mpaka onse amene anatsala+ ndiponso amene anabisala pamaso panu atawonongedwa. 21 Musachite nawo mantha chifukwa Yehova Mulungu wanu, Mulungu wamphamvu komanso wochititsa mantha,+ ali pakati panu.+

22 Yehova Mulungu wanu adzathamangitsira mitundu imeneyi kutali ndi inu, kuichotsa pamaso panu pangʼonopangʼono.+ Sadzakulolani kuti muiwononge mofulumira, kuopera kuti zilombo zakutchire zingachuluke nʼkukuwonongani. 23 Yehova Mulungu wanu adzawapereka kwa inu ndipo mudzawagonjetsa mobwerezabwereza mpaka onse atatha.+ 24 Adzapereka mafumu awo mʼmanja mwanu,+ ndipo inu mudzafafanize mayina awo padziko lapansi.+ Palibe munthu amene adzalimbane ndi inu+ mpaka mutawawononga.+ 25 Mudzawotche pamoto zifaniziro zogoba za milungu yawo.+ Musadzalakelake siliva ndi golide wawo kapena kutenga zinthu zimenezi kuti zikhale zanu,+ kuopera kuti zingakutchereni msampha, chifukwa zinthu zimenezi ndi zonyansa kwa Yehova Mulungu wanu.+ 26 Musabweretse mʼnyumba mwanu zinthu zonyansa kuti nanunso musakhale oyenera kuwonongedwa mofanana ndi zinthuzo. Muzinyansidwa nazo kwambiri komanso kuipidwa nazo chifukwa zinthu zimenezi ndi zoyenera kuwonongedwa.”

8 “Muonetsetse kuti mukusunga lamulo lililonse limene ndikukupatsani lero, kuti mupitirize kukhala ndi moyo+ komanso kuti muchuluke, nʼkupita kukatenga dziko limene Yehova analumbira kwa makolo anu.+ 2 Muzikumbukira njira yaitali imene Yehova Mulungu wanu anakuyendetsani mʼchipululu zaka 40 zonsezi.+ Iye anakuyendetsani mʼchipululu kuti akuphunzitseni kudzichepetsa komanso kukuyesani+ pofuna kudziwa zimene zinali mumtima mwanu,+ kuti aone ngati mungasunge malamulo ake kapena ayi. 3 Anakuphunzitsani kudzichepetsa pokulolani kuti mukhale ndi njala+ nʼkukudyetsani mana,+ amene inu kapena makolo anu sankawadziwa. Anachita zimenezi kuti mudziwe kuti munthu sangakhale ndi moyo ndi chakudya chokha, koma ndi mawu alionse ochokera mʼkamwa mwa Yehova.+ 4 Zovala zimene munavala sizinathe ndipo mapazi anu sanatupe pa zaka 40 zimenezi.+ 5 Inu mukudziwa bwino mumtima mwanu kuti Yehova Mulungu wanu ankakulangizani, ngati mmene bambo amalangizira mwana wake.+

6 Tsopano muzisunga malamulo a Yehova Mulungu wanu poyenda mʼnjira zake ndi kumuopa. 7 Chifukwa Yehova Mulungu wanu akukulowetsani mʼdziko labwino,+ dziko la mitsinje ya madzi,* akasupe ndi madzi ochuluka amene akuyenda mʼzigwa ndi mʼdera lamapiri, 8 dziko la tirigu, balere, mphesa, mitengo ya mkuyu ndi makangaza,*+ dziko la maolivi opangira mafuta ndiponso la uchi,+ 9 mʼdziko limene simudzasowa chakudya komanso simudzasowa chilichonse, dziko limene miyala yake amapangira zitsulo, limenenso mʼmapiri ake mudzakumbamo kopa.*

10 Mukadzadya nʼkukhuta, mudzatamande Yehova Mulungu wanu chifukwa cha dziko labwino limene wakupatsani.+ 11 Samalani kuti musaiwale Yehova Mulungu wanu polephera kusunga malamulo, zigamulo ndi malangizo ake amene ndikukupatsani lero. 12 Mukadzadya nʼkukhuta, kumanga nyumba zabwino nʼkukhalamo,+ 13 ngʼombe zanu ndi nkhosa zanu nʼkuchuluka, siliva ndi golide wanu nʼkuwonjezeka ndiponso nʼkukhala ndi zinthu zochuluka, 14 musakalole kuti mtima wanu ukayambe kunyada+ nʼkukuchititsani kuiwala Yehova Mulungu wanu amene anakutulutsani mʼdziko la Iguputo, mʼnyumba yaukapolo,+ 15 amene anakuyendetsani mʼchipululu chachikulu ndi chochititsa mantha,+ chokhala ndi njoka zapoizoni, zinkhanira ndiponso nthaka youma yopanda madzi. Iye anachititsa kuti madzi atuluke pamwala wolimba,+ 16 anakudyetsani mana+ mʼchipululu, chakudya chimene makolo anu sankachidziwa, kuti akuphunzitseni kudzichepetsa+ komanso kukuyesani kuti mʼtsogolo zinthu zidzakuyendereni bwino.+ 17 Ngati mumtima mwanu munganene kuti, ‘Chuma ichi ndachipeza chifukwa cha ntchito ya manja anga komanso mphamvu zanga,’+ 18 muzikumbukira kuti ndi Yehova Mulungu wanu amene amakupatsani mphamvu kuti mupeze chuma,+ pofuna kusunga pangano lake limene analumbira kwa makolo anu, ngati mmene zilili lero.+

19 Koma mukadzaiwala Yehova Mulungu wanu nʼkutsatira milungu ina, kuitumikira ndiponso kuigwadira, ndikukuchenjezani lero kuti anthu inu mudzatha ndithu.+ 20 Mudzatheratu mofanana ndi mitundu imene Yehova akuiwononga pamaso panu, chifukwa simunamvere mawu a Yehova Mulungu wanu.”+

9 “Tamverani Aisiraeli inu, lero mukuwoloka Yorodano+ kulowa mʼdziko limene mukukalilanda kwa mitundu ikuluikulu ndi yamphamvu kuposa inuyo.+ Mukukalanda mizinda ikuluikulu yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri yofika kumwamba,*+ 2 yokhalanso ndi anthu amphamvu ndi aatali, ana a Anaki,+ amene inu mukuwadziwa ndipo munamva anthu akunena za iwo kuti, ‘Ndani angaime pamaso pa ana a Anaki?’ 3 Choncho mudziwe lero kuti Yehova Mulungu wanu awoloka patsogolo panu.+ Iye ndi moto wowononga+ ndipo adzawawononga. Adzawagonjetsa inu mukuona kuti mudzawathamangitse* mwamsanga ndi kuwawononga, mogwirizana ndi zimene Yehova anakulonjezani.+

4 Yehova Mulungu wanu akadzawathamangitsa pamaso panu musadzanene mumtima mwanu kuti, ‘Yehova watilowetsa mʼdziko lino kuti tilitenge kukhala lathu, chifukwa chakuti ndife olungama.’+ Mʼmalomwake, Yehova akuthamangitsa mitundu iyi pamaso panu chifukwa choti ndi yoipa.+ 5 Sikuti mukulowa mʼdzikoli kukalitenga kukhala lanu chifukwa choti ndinu olungama kapena chifukwa choti ndinu owongoka mtima. Koma Yehova Mulungu wanu akuthamangitsira mitundu imeneyi kutali ndi inu,+ chifukwa choti ndi yoipa, ndiponso kuti Yehova akwaniritse mawu onse amene analumbirira makolo anu Abulahamu,+ Isaki+ ndi Yakobo.+ 6 Choncho mudziwe kuti Yehova Mulungu wanu sakukupatsani dziko labwinoli chifukwa choti ndinu olungama, paja ndinu anthu ouma khosi.+

7 Kumbukirani ndipo musamaiwale mmene munakwiyitsira Yehova Mulungu wanu mʼchipululu.+ Anthu inu mwakhala mukupandukira Yehova kuyambira tsiku limene munachoka mʼdziko la Iguputo mpaka kudzafika malo ano.+ 8 Ngakhale ku Horebe, inu munakwiyitsa Yehova moti Yehova anakukwiyirani kwambiri ndipo ankafuna kukuwonongani.+ 9 Nditakwera mʼphiri kukalandira miyala iwiri yosema,+ miyala ya pangano limene Yehova anachita ndi inu,+ ndinakhala mʼphirimo masiku 40, masana ndi usiku,+ ndipo sindinadye chakudya kapena kumwa madzi. 10 Kenako Yehova anandipatsa miyala iwiri yosema imene Mulungu analembapo ndi chala chake. Pamiyala imeneyi panali mawu onse amene Yehova analankhula nanu mʼphiri, kuchokera mʼmoto, pa tsiku limene munasonkhana kumeneko.+ 11 Patadutsa masiku 40, masana ndi usiku, Yehova anandipatsa miyala iwiriyo, miyala ya pangano. 12 Ndiyeno Yehova anandiuza kuti, ‘Nyamuka, tsika mofulumira mʼphiri muno, chifukwa anthu ako amene unawatulutsa ku Iguputo achita zinthu zoipa.+ Apatuka mofulumira panjira imene ndinawalamula kuti aziyendamo. Adzipangira chifaniziro chopangidwa ndi chitsulo.’*+ 13 Kenako Yehova anandiuza kuti, ‘Ndawaona anthu awa ndipo ndaona kuti ndi anthu ouma khosi.+ 14 Ndisiye kuti ndiwawononge nʼkufafaniza dzina lawo pansi pa thambo, ndipo ndikupange iweyo kukhala mtundu wamphamvu komanso waukulu kwambiri kuposa iwowo.’+

15 Kenako ndinatembenuka nʼkutsika mʼphirimo pa nthawi imene phirilo linkayaka moto,+ ndipo miyala iwiri ya pangano inali mʼmanja mwanga.+ 16 Nditayangʼana, ndinaona kuti mwachimwira Yehova Mulungu wanu. Munali mutadzipangira mwana wa ngʼombe wachitsulo.* Munali mutapatuka mofulumira panjira imene Yehova anakulamulani kuti muziyendamo.+ 17 Choncho ndinatenga miyala iwiriyo nʼkuiponya pansi mwamphamvu ndi manja anga, ndipo ndinaiswa inu mukuona.+ 18 Zitatero ndinkadzigwetsa pansi pamaso pa Yehova kwa masiku 40, masana ndi usiku, ngati mmene ndinachitira poyamba. Sindinkadya chakudya kapena kumwa madzi+ chifukwa cha machimo anu onse amene munachita pochita zinthu zoipa pamaso pa Yehova nʼkumukhumudwitsa. 19 Ndinachita mantha chifukwa cha mkwiyo waukulu umene Yehova anali nawo pa inu,+ moti ankafuna kukuwonongani. Koma pa nthawi imeneyinso Yehova anandimvetsera.+

20 Yehova anakwiyira kwambiri Aroni, moti ankafuna kumuwononga,+ koma ine ndinapembedzera Mulungu pa nthawi imeneyonso kuti asawononge Aroni. 21 Ndiyeno ndinatenga mwana wa ngʼombeyo, amene munachimwa chifukwa chomupanga,+ ndipo ndinamuwotcha pamoto. Kenako ndinamuphwanya, nʼkumupera mpaka kukhala wosalala ngati fumbi, ndipo ndinawaza fumbilo mumtsinje umene unkachokera mʼphirimo.+

22 Kuwonjezera pamenepo, munaputanso mkwiyo wa Yehova ku Tabera,+ ku Masa+ ndi ku Kibiroti-hatava.+ 23 Yehova atakutumani kuchokera ku Kadesi-barinea+ kuti, ‘Pitani mukatenge dziko limene ndidzakupatsani kuti likhale lanu,’ inu munapandukiranso lamulo la Yehova Mulungu wanu,+ ndipo simunasonyeze chikhulupiriro+ mwa iye komanso simunamvere mawu ake. 24 Mwakhala mukupandukira Yehova kuyambira tsiku limene ndinakudziwani.

25 Choncho ndinkadzigwetsa pansi pamaso pa Yehova kwa masiku 40, masana ndi usiku.+ Ndinkadzigwetsa chifukwa Yehova ananena kuti akufuna kukuwonongani. 26 Ine ndinayamba kupembedzera Yehova nʼkunena kuti, ‘Yehova Ambuye Wamkulu Koposa, musawononge anthu anu. Anthuwa ndi anu,*+ amene munawawombola ndi mphamvu yanu ndipo munawatulutsa mu Iguputo ndi dzanja lamphamvu.+ 27 Kumbukirani atumiki anu Abulahamu, Isaki ndi Yakobo.+ Khululukirani anthuwa chifukwa cha unkhutukumve wawo, kuipa kwawo ndiponso tchimo lawo.+ 28 Mukapanda kutero, anthu amʼdziko limene munatitulutsamo adzanena kuti: “Yehova sanathe kuwalowetsa mʼdziko limene anawalonjeza komanso chifukwa chakuti ankadana nawo, anawatulutsa kuti akawaphe mʼchipululu.”+ 29 Iwo ndi anthu anu komanso chuma chanu chapadera,*+ anthu amene munawatulutsa ndi mphamvu zanu zazikulu ndi dzanja lanu lotambasula.’”+

10 “Pa nthawi imeneyo Yehova anandiuza kuti, ‘Useme miyala iwiri yofanana ndi yoyamba ija+ komanso upange likasa lamatabwa. Ukatero ukwere mʼphiri muno kwa ine. 2 Pamiyalayo ndidzalembapo mawu amene anali pamiyala yoyamba ija, imene unaiswa, ndipo udzaiike mʼlikasalo.’ 3 Choncho ndinapanga likasa la mtengo wa mthethe nʼkusema miyala iwiri yofanana ndi yoyamba ija. Kenako ndinakwera mʼphiri, miyala iwiriyo ili mʼmanja mwanga.+ 4 Ndiyeno analemba pamiyalayo mawu amene analemba poyamba aja,+ Malamulo Khumi,*+ amene Yehova anakuuzani paphiri kuchokera mʼmoto,+ pa tsiku limene munasonkhana kuphiri.+ Atatero, Yehova anandipatsa miyalayo. 5 Kenako ndinatembenuka nʼkutsika mʼphirimo+ ndipo ndinaika miyala iwiriyo mʼlikasa limene ndinapanga. Mpaka pano miyalayo idakali momwemo, mogwirizana ndi zimene Yehova anandilamula.

6 Zitatero Aisiraeli anachoka ku Beeroti Bene-yaakana kupita ku Mosera. Kumeneku nʼkumene Aroni anafera ndipo anamuikanso komweko.+ Mwana wake Eleazara anayamba kutumikira monga wansembe mʼmalo mwa Aroniyo.+ 7 Ndiyeno ananyamuka pamalo amenewo kupita ku Gudigoda. Anachokanso ku Gudigoda kupita ku Yotibata,+ dziko lokhala ndi mitsinje ya madzi.*

8 Pa nthawi imeneyo, Yehova anapatula fuko la Levi+ kuti lizinyamula likasa la pangano la Yehova,+ liziima pamaso pa Yehova nʼkumamutumikira komanso kuti lizidalitsa anthu mʼdzina lake+ ngati mmene akuchitira mpaka lero. 9 Nʼchifukwa chake fuko la Levi silinapatsidwe gawo kapena cholowa ngati abale awo. Cholowa chawo ndi Yehova, mogwirizana ndi zimene Yehova Mulungu wanu anawauza.+ 10 Ine ndinakhala mʼphirimo kwa masiku 40, masana ndi usiku,+ ngati mmene ndinachitira poyamba paja. Pa nthawi imeneyinso Yehova anandimvetsera.+ Yehova sankafuna kukuwonongani. 11 Kenako Yehova anandiuza kuti, ‘Tsogolera anthuwa ndipo mukonzekere ulendo, kuti akalowe nʼkutenga dziko limene ndinalumbira kwa makolo awo kuti ndidzawapatsa.’+

12 Tsopano Aisiraeli inu, kodi Yehova Mulungu wanu akufuna kuti muzichita chiyani?+ Akufuna kuti muzichita izi: muziopa Yehova Mulungu wanu,+ muziyenda mʼnjira zake zonse,+ muzikonda ndi kutumikira Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse komanso moyo wanu wonse,+ 13 ndiponso kuti muzisunga malamulo a Yehova ndi malangizo ake amene ndikukupatsani lero, kuti zinthu zikuyendereni bwino.+ 14 Taonani, kumwamba ndi kwa Yehova Mulungu wanu, ngakhale kumwamba kwa kumwambako* komanso dziko lapansi ndi zonse zili mmenemo zonsezo ndi zake.+ 15 Koma Yehova anayandikira kwa makolo anu okha nʼkuwasonyeza chikondi chake, ndipo wasankha inuyo mbadwa zawo+ pakati pa anthu onse, ngati mmene mulili lero. 16 Tsopano muyeretse* mitima yanu+ ndipo musakhalenso ankhutukumve.*+ 17 Chifukwa Yehova Mulungu wanu ndi Mulungu wa milungu+ ndi Mbuye wa ambuye. Iye ndi Mulungu wamkulu, wamphamvu ndi woopsa, amene sakondera munthu aliyense+ ndipo salandira chiphuphu. 18 Iye amachitira chilungamo ana amasiye ndi akazi amasiye,+ ndipo amakonda mlendo+ moti amamupatsa chakudya ndi zovala. 19 Inunso muzikonda mlendo, chifukwa nanunso munali alendo mʼdziko la Iguputo.+

20 Yehova Mulungu wanu muzimuopa, muzimutumikira,+ muzikhala naye pafupi kwambiri komanso muzilumbira pa dzina lake. 21 Iye ndi amene muyenera kumutamanda.+ Iyeyo ndi Mulungu wanu amene wakuchitirani zinthu zazikulu ndi zochititsa mantha zonsezi, zimene mwaziona ndi maso anu.+ 22 Makolo anu anapita ku Iguputo ndi anthu 70,+ koma pano Yehova Mulungu wanu wakuchulukitsani ngati nyenyezi zakumwamba.”+

11 “Muzikonda Yehova Mulungu wanu+ ndipo nthawi zonse muzichita zofuna zake, kutsatira malangizo ake, zigamulo zake komanso malamulo ake. 2 Inuyo mukudziwa kuti lero ndikulankhula ndi inu, osati ndi ana anu amene sakudziwa komanso sanaone chilango cha Yehova Mulungu wanu,+ ukulu wake,+ dzanja lake lamphamvu+ komanso mkono wake wotambasula. 3 Iwo sanaone zizindikiro ndi zinthu zimene anachita mʼdziko la Iguputo kwa Farao mfumu ya Iguputo komanso mʼdziko lake lonse.+ 4 Sanaonenso zimene Mulungu anachitira gulu la asilikali a ku Aiguputo, mahatchi a Farao ndi magaleta ake ankhondo, amene anamira mʼmadzi a mʼNyanja Yofiira pamene ankakuthamangitsani, ndipo Yehova anawawononga nʼkutheratu.+ 5 Iwo sanaone zimene Mulungu wakuchitirani mʼchipululu mpaka kudzafika malo ano, 6 kapena zimene anachitira Datani ndi Abiramu, ana a Eliyabu, mwana wa Rubeni, pamene dziko linatsegula pakamwa pake nʼkuwameza pamodzi ndi mabanja awo, matenti awo ndi chamoyo chilichonse chimene anali nacho. Dziko linawameza Aisiraeli onse akuona.+ 7 Inu munaona ndi maso anu zinthu zonse zazikulu zimene Yehova anachita.

8 Muzisunga malamulo onse amene ndikukupatsani lero, kuti mukhale amphamvu nʼkulowa mʼdziko limene mukuwolokerako kuti mukalitenge kukhala lanu, 9 kutinso mukhale ndi moyo nthawi yaitali+ mʼdziko limene Yehova analumbira kwa makolo anu kuti adzawapatsa iwowo ndi mbadwa* zawo,+ dziko loyenda mkaka ndi uchi.+

10 Dziko limene mukupita kukalitenga kuti likhale lanu, si lofanana ndi dziko la Iguputo limene munatulukamo. Kumeneko munkafesa mbewu zanu nʼkumazithirira ndi mapazi* anu ngati kuti mukuthirira dimba la ndiwo zamasamba. 11 Koma dziko limene mwatsala pangʼono kuwolokerako nʼkukalitenga kuti likhale lanu ndi dziko lamapiri ndi zigwa.+ Limamwa madzi a mvula amene amagwa kuchokera kumwamba.+ 12 Limeneli ndi dziko limene Yehova Mulungu wanu akulisamalira. Nthawi zonse maso a Yehova Mulungu wanu amakhala padziko limeneli, kuyambira kumayambiriro kwa chaka mpaka kumapeto.

13 Ndiyeno mukadzamvera mokhulupirika malamulo anga amene ndikukupatsani lero, komanso kukonda Yehova Mulungu wanu nʼkumamutumikira ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse,+ 14 ndidzakupatsaninso mvula pa nthawi yake mʼdziko lanu, mvula yoyambirira ndi mvula yomaliza, ndipo mudzakolola mbewu zanu nʼkukhala ndi vinyo watsopano komanso mafuta.+ 15 Ndidzameretsa msipu mʼdziko lanu kuti ziweto zanu zidye, ndipo inu mudzadya nʼkukhuta.+ 16 Samalani kuti mitima yanu isakopeke nʼkupatuka ndi kuyamba kulambira milungu ina nʼkumaiweramira.+ 17 Mukatero mkwiyo wa Yehova udzakuyakirani ndipo iye adzatseka kumwamba moti mvula sidzagwa+ komanso nthaka sidzapereka zokolola zake. Zikadzatero mudzatha mofulumira mʼdziko labwino limene Yehova akukupatsani.+

18 Mawu angawa muwasunge mʼmitima yanu ndipo muziwatsatira pa moyo wanu. Muwamange padzanja lanu kuti muziwakumbukira ndipo akhale ngati chomanga pachipumi panu.*+ 19 Muziphunzitsa ana anu mawu amenewa, ndipo muzilankhula nawo mawuwa mukakhala pansi mʼnyumba mwanu, mukamayenda pamsewu, mukamagona komanso mukadzuka.+ 20 Muziwalemba pamafelemu a nyumba zanu ndi pamageti a mizinda yanu, 21 kuti inuyo ndi ana anu mukhale ndi moyo wautali+ mʼdziko limene Yehova analumbira kwa makolo anu kuti adzawapatsa,+ kwa nthawi yonse imene thambo lidzakhale pamwamba pa dziko lapansi.

22 Mukasunga mosamala malamulo onsewa amene ndikukupatsani nʼkumawatsatira, kukonda Yehova Mulungu wanu,+ kuyenda mʼnjira zake zonse ndi kumʼmamatira,+ 23 Yehova adzathamangitsa mitundu yonseyi pamaso panu,+ ndipo mitundu yamphamvu ndi yaikulu kuposa inu mudzailanda dziko.+ 24 Malo alionse amene mapazi anu adzaponde adzakhala anu.+ Malire a dziko lanu adzayambira kuchipululu kukafika ku Lebanoni, kuyambira ku mtsinje wa Firate, kukafika kunyanja yakumadzulo.*+ 25 Palibe munthu amene adzalimbane nanu.+ Yehova Mulungu wanu adzachititsa dziko lonse limene mudzayendemo kugwidwa ndi mantha aakulu ndipo adzakuopani,+ mogwirizana ndi zimene anakulonjezani.

26 Onani, lero ndikuika dalitso ndi temberero pamaso panu:+ 27 mudzalandira dalitsoli mukadzamvera malamulo a Yehova Mulungu wanu, amene ndikukupatsani lero,+ 28 ndipo mudzalandira temberero limeneli ngati simudzamvera malamulo a Yehova Mulungu wanu,+ nʼkupatuka panjira imene ndikukulamulani lero kuti muziyendamo nʼkuyamba kutsatira milungu imene simukuidziwa.

29 Yehova Mulungu wanu akadzakulowetsani mʼdziko limene mukupita kukalitenga kuti likhale lanu, mukatchule dalitsoli paphiri la Gerizimu ndipo temberero mukalitchulire* paphiri la Ebala.+ 30 Pajatu mapiri amenewa ali kutsidya lina la mtsinje wa Yorodano chakumadzulo,* mʼdziko la Akanani amene akukhala ku Araba, moyangʼanizana ndi Giligala, pafupi ndi mitengo ikuluikulu ya ku More.+ 31 Inu muwoloka Yorodano nʼkukalowa mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani kuti likhale lanu.+ Mukakalitenga nʼkuyamba kukhalamo, 32 muzikaonetsetsa kuti mukusunga malamulo ndi zigamulo zonse zimene ndikuika pamaso panu lero.”+

12 “Awa ndi malangizo ndi zigamulo zimene muyenera kutsatira mosamala, masiku onse amene mudzakhale mʼdziko limene Yehova Mulungu wa makolo anu adzakupatseni kuti likhale lanu. 2 Mukawonongeretu malo onse amene mitundu imene mukukailanda dziko lawo imatumikirirapo milungu yawo,+ kaya ndi pamapiri ataliatali, pazitunda ndi pansi pa mtengo uliwonse waukulu wa masamba obiriwira. 3 Mukagwetse maguwa awo ansembe nʼkuphwanya zipilala zawo zopatulika.+ Mukawotche mizati yawo yopatulika* nʼkudula zifaniziro zogoba za milungu yawo,+ ndipo mukachotseretu mayina awo pamalo amenewo.+

4 Musamalambire Yehova Mulungu wanu mwa njira imeneyi.+ 5 Mʼmalomwake, mudzafunefune Yehova Mulungu wanu pamalo alionse amene adzasankhe kuti aikepo dzina lake komanso malo amene azidzakhala pakati pa mafuko anu onse, ndipo muzidzapita kumeneko.+ 6 Nsembe zanu zopsereza ndi nsembe zina, zopereka zanu za chakhumi,*+ chopereka chochokera mʼmanja mwanu,+ nsembe zimene mukupereka pokwaniritsa lonjezo, nsembe zanu zaufulu,+ ana oyamba kubadwa a ngʼombe ndi a nkhosa zanu,+ zonsezi muzidzapita nazo kumalo amenewo.+ 7 Inuyo ndi mabanja anu muzidzadya zimenezi kumalo amenewo pamaso pa Yehova Mulungu wanu,+ ndipo muzidzasangalala ndi zochita zanu zonse+ chifukwa Yehova Mulungu wanu wakudalitsani.

8 Musamakachite zimene tikuchita kuno lero, aliyense kumangochita zimene akuona kuti nʼzabwino,* 9 chifukwa simunafike kumalo anu a mpumulo+ nʼkulandira cholowa chimene Yehova Mulungu wanu akukupatsani. 10 Mukawoloka Yorodano+ nʼkukakhala mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani kuti likhale lanu, adzakutetezani kwa adani anu onse okuzungulirani, ndipo mudzakhala otetezeka.+ 11 Muzidzabweretsa zinthu zonse zimene ndikukulamulani kumalo amene Yehova Mulungu wanu adzasankhe kuti kukhale dzina lake.+ Muzidzabweretsa nsembe zanu zopsereza ndi nsembe zina, zopereka zanu za chakhumi,+ chopereka chochokera mʼmanja mwanu ndi nsembe zonse zimene mukupereka pokwaniritsa lonjezo limene munachita kwa Yehova. 12 Mudzasangalala pamaso pa Yehova Mulungu wanu,+ inuyo ndi ana anu aamuna, ana anu aakazi, akapolo anu aamuna, akapolo anu aakazi ndi Mlevi amene akukhala mumzinda wanu,* chifukwa iye sanapatsidwe gawo kapena cholowa mofanana ndi inu.+ 13 Samalani kuti musamadzapereke nsembe zanu zopsereza pamalo ena alionse amene mungaone.+ 14 Muzidzapereka nsembe zanu zopsereza pamalo amene Yehova adzasankhe mʼdera limodzi mwa madera a mafuko anu, ndipo pamalo amenewo muzidzachita chilichonse chimene ndakulamulani.+

15 Ngati mukufuna kudya nyama, mungathe kupha chiweto chanu nʼkudya nyama yake nthawi iliyonse,+ mogwirizana ndi madalitso amene Yehova Mulungu wanu wakupatsani mʼmizinda yanu yonse.* Munthu wodetsedwa komanso munthu wosadetsedwa angathe kudya nyamayo, ngati mmene mungadyere insa ndi mbawala. 16 Koma musamadye magazi ake.+ Muziwathira pansi ngati madzi.+ 17 Simudzaloledwa kudyera mʼmizinda yanu* chakhumi cha mbewu zanu, vinyo wanu watsopano, mafuta anu, ana oyamba kubadwa a ngʼombe zanu ndi a nkhosa zanu,+ iliyonse mwa nsembe zimene mukupereka pokwaniritsa lonjezo limene mwachita, nsembe zanu zaufulu kapena chopereka chochokera mʼmanja mwanu. 18 Koma muzidzadya zinthu zimenezi pamaso pa Yehova Mulungu wanu, pamalo amene Yehova Mulungu wanu adzasankhe.+ Muzidzadya zinthuzi inuyo, mwana wanu wamwamuna, mwana wanu wamkazi, kapolo wanu wamwamuna, kapolo wanu wamkazi ndi Mlevi amene akukhala mumzinda wanu.* Ndipo muzidzasangalala pamaso pa Yehova Mulungu wanu ndi zochita zanu zonse. 19 Samalani kuti musakanyalanyaze Mlevi+ kwa nthawi yonse imene mukakhale mʼdzikolo.

20 Yehova Mulungu wanu akadzawonjezera dziko lanu+ mogwirizana ndi zimene anakulonjezani,+ ndipo inu nʼkunena kuti, ‘Ndikufuna kudya nyama,’ chifukwa mukulakalaka kudya nyama, nthawi iliyonse imene mwalakalaka kudya nyama muzidzadya.+ 21 Ngati malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankhe kuikapo dzina lake+ adzakhale kutali kwambiri ndi inu, muzidzapha zina mwa ngʼombe zanu kapena nkhosa zanu zimene Yehova wakupatsani, mogwirizana ndi zimene ndakulamulani, ndipo nyamazo muzidzadyera mumzinda wanu* nthawi iliyonse imene mukufuna. 22 Mungathe kuidya ngati mmene mungadyere insa ndi mbawala.+ Munthu wodetsedwa komanso munthu wosadetsedwa angathe kudya nyamayo. 23 Koma mungokhala otsimikiza mtima kuti musadye magazi,+ chifukwa magazi ndi moyo,+ ndipo musamadye nyama limodzi ndi moyo wake. 24 Musamadye magazi. Muziwathira pansi ngati madzi.+ 25 Musamadye magazi, kuti zinthu zikuyendereni bwino inuyo ndi ana anu obwera mʼmbuyo mwanu, chifukwa choti mukuchita zinthu zoyenera pamaso pa Yehova. 26 Popita kumalo amene Yehova adzasankhe, muzidzatenga zinthu zanu zokha zopatulika komanso zinthu zoti mukapereke nsembe pokwaniritsa lonjezo limene munachita. 27 Kumeneko muzikapereka nsembe zanu zopsereza, nyama ndi magazi,+ paguwa lansembe la Yehova Mulungu wanu. Magazi a nsembe zanu azidzathiridwa pansi pafupi ndi guwa lansembe+ la Yehova Mulungu wanu, koma nyamayo mungathe kuidya.

28 Muzionetsetsa kuti mukumvera mawu onsewa amene ndikukuuzani, kuti nthawi zonse zinthu zizikuyenderani bwino, inuyo ndi ana anu obwera mʼmbuyo mwanu, chifukwa choti mukuchita zabwino ndi zoyenera pamaso pa Yehova Mulungu wanu.

29 Yehova Mulungu wanu akadzawononga mitundu imene mukupita kukailanda dziko,+ inuyo nʼkuyamba kukhala mʼdziko lawolo, 30 mukasamale kuti musakagwidwe mumsampha wawo, pambuyo poti awonongedwa ndi kuchotsedwa pamaso panu. Musakafunse zokhudza milungu yawo kuti, ‘Kodi mitundu imeneyi inkatumikira bwanji milungu yawo? Inenso ndichita zomwezo.’+ 31 Musamalambire Yehova Mulungu wanu mwa njira imeneyi, chifukwa iwo amachitira milungu yawo zinthu zonse zonyansa zimene Yehova amadana nazo. Iwo amafika ngakhale powotcha ana awo aamuna ndi aakazi pamoto kuti ikhale nsembe kwa milungu yawo.+ 32 Muzionetsetsa kuti mukutsatira mawu onse amene ndikukuuzani.+ Musawonjezerepo kapena kuchotsapo kalikonse.”+

13 “Pakati panu pakapezeka mneneri kapena wolosera za mʼtsogolo pogwiritsa ntchito maloto nʼkukupatsani chizindikiro kapena kulosera china chake, 2 ndipo chizindikiro kapena zimene analoserazo zachitikadi, kenako iye nʼkunena kuti, ‘Tiyeni titsatire milungu ina,’ milungu imene simukuidziwa, ‘ndipo tiitumikire,’ 3 musamvere mawu a mneneriyo kapena woloserayo,+ chifukwa Yehova Mulungu wanu akukuyesani+ kuti adziwe ngati mumakonda Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse komanso moyo wanu wonse.+ 4 Muzitsatira Yehova Mulungu wanu, muzimuopa, muzisunga malamulo ake, muzimvera mawu ake ndipo iye ndi amene muyenera kumutumikira komanso kumumamatira.+ 5 Koma mneneri kapena woloserayo muzimupha,+ chifukwa akulimbikitsa anthu kuti azipandukira Yehova Mulungu wanu amene anakutulutsani mʼdziko la Iguputo komanso kukuwombolani mʼnyumba yaukapolo. Munthu ameneyo akufuna akupatutseni panjira imene Yehova Mulungu wanu anakulamulani kuti muziyendamo. Choncho muzichotsa woipayo pakati panu.+

6 Mchimwene wanu, amene ndi mwana wamwamuna wa mayi anu, kapena mwana wanu wamwamuna, mwana wanu wamkazi, mkazi wanu wokondedwa kapena mnzanu wapamtima, akayesa kukukopani mwachinsinsi pokuuzani kuti, ‘Tiyeni tikatumikire milungu ina,’+ milungu imene inuyo kapena makolo anu sankaidziwa, 7 kaya ndi milungu ya anthu amene akuzungulirani, amene akukhala pafupi ndi inu kapena amene akukhala kutali ndi inu, kuchokera kumalekezero ena a dziko kukafika kumalekezero ena, 8 musavomere kuchita zimene akufunazo kapena kumumvera.+ Musamumvere chisoni kapena kumuchitira chifundo kapenanso kumuteteza. 9 Koma muzimupha ndithu.+ Dzanja lanu lizikhala loyamba kumʼponya miyala kuti afe, ndipo anthu ena onse azibwera pambuyo.+ 10 Muzimuponya miyala kuti afe,+ chifukwa amafuna akuchotseni kwa Yehova Mulungu wanu, amene anakutulutsani mʼdziko la Iguputo, mʼnyumba yaukapolo. 11 Zikadzatero Aisiraeli onse adzamva nʼkuchita mantha, ndipo sadzachitanso chinthu choipa chilichonse ngati chimenechi pakati panu.+

12 Mukadzamva mu umodzi mwa mizinda yanu, imene Yehova Mulungu wanu wakupatsani kuti muzikhalamo kuti, 13 ‘Pakati panu papezeka anthu opanda pake amene akufuna kusocheretsa anthu mumzinda wawo, ponena kuti: “Tiyeni tikatumikire milungu ina,” milungu imene inu simukuidziwa,’ 14 muzifufuza mosamala kwambiri komanso muzifunsa ena za nkhaniyo.+ Ndiye zikatsimikizirika kuti ndi zoonadi kuti chinthu chonyansachi chachitika pakati panu, 15 muzipha ndithu anthu amumzindawo ndi lupanga.+ Muziwononga ndi lupanga mzindawo komanso chilichonse chimene chili mmenemo, kuphatikizapo ziweto zake.+ 16 Kenako muzisonkhanitsa zinthu zonse zimene mwapeza mumzindawo, pakati pa bwalo lake nʼkuwotcha mzindawo ndi moto. Ndipo zinthu zimene munapeza mumzindawo zidzakhala nsembe yopsereza yoperekedwa kwa Yehova Mulungu wanu. Mzindawo udzakhale bwinja mpaka kalekale ndipo usadzamangidwenso. 17 Dzanja lanu lisatenge chinthu chilichonse choyenera kuwonongedwa,+ kuti mkwiyo woyaka moto wa Yehova usiye kukuyakirani ndiponso kuti akuchitireni chifundo, kukumverani chisoni ndi kukuchulukitsani, mogwirizana ndi zimene analumbira kwa makolo anu.+ 18 Choncho muzimvera* Yehova Mulungu wanu, posunga malamulo ake onse amene ndikukupatsani lero, mukatero mudzachita zinthu zoyenera pamaso pa Yehova Mulungu wanu.”+

14 “Inu ndinu ana a Yehova Mulungu wanu. Musamadzichekecheke+ kapena kumeta nsidze zanu* chifukwa cha anthu akufa.+ 2 Chifukwa ndinu anthu oyera+ kwa Yehova Mulungu wanu, ndipo Yehova wakusankhani kuti mukhale anthu ake, chuma chake chapadera, pa anthu onse okhala padziko lapansi.+

3 Musamadye chinthu chilichonse chonyansa.+ 4 Nyama zimene mungathe kudya+ ndi izi: ngʼombe, nkhosa, mbuzi, 5 mbawala, insa, ngondo, mbuzi yakuthengo, mphalapala, nkhosa yakuthengo ndi nkhosa yamʼmapiri. 6 Mungathe kudya nyama iliyonse ya ziboda zogawanika, zokhala ndi mpata pakati, imenenso imabzikula. 7 Koma musamadye nyama izi zokha zimene zimabzikula kapena zimene zili ndi ziboda zogawanika: ngamila, kalulu ndi mbira, chifukwa zimabzikula koma si zogawanika ziboda. Nyama zimenezi nʼzodetsedwa kwa inu.+ 8 Musamadyenso nkhumba chifukwa ndi ya ziboda zogawanika koma sibzikula. Imeneyi ndi yodetsedwa kwa inu. Musamadye nyama yake kapena kuikhudza ikafa.

9 Pa zinthu zonse zokhala mʼmadzi, zimene mungadye ndi izi: Chilichonse chimene chili ndi zipsepse ndi mamba mungadye.+ 10 Koma musamadye chilichonse chimene chilibe zipsepse ndi mamba. Chimenecho nʼchodetsedwa kwa inu.

11 Mungathe kudya mbalame iliyonse yosadetsedwa. 12 Koma mbalame izi ndi zimene simuyenera kudya: chiwombankhanga, nkhwazi, muimba wakuda,+ 13 mphamba wofiira, mphamba wakuda ndi mtundu uliwonse wa kamtema. 14 Simuyeneranso kudya mtundu uliwonse wa khwangwala, 15 nthiwatiwa, kadzidzi, kakowa ndi mtundu uliwonse wa kabawi, 16 nkhwezule, mantchichi, tsekwe, 17 vuwo, muimba, chiswankhono, 18 dokowe, sadzu, mleme ndi mtundu uliwonse wa chimeza. 19 Tizilombo tonse ta mapiko timene timapezeka tambiri nʼtodetsedwanso kwa inu. Timeneti simuyenera kudya. 20 Cholengedwa chilichonse chouluka chosadetsedwa mungadye.

21 Musamadye nyama iliyonse imene mwaipeza yakufa.+ Mungapatse mlendo amene akukhala mumzinda wanu* kuti adye, kapena mungathe kuigulitsa kwa mlendo chifukwa inu ndinu anthu oyera kwa Yehova Mulungu wanu.

Musamawiritse mwana wa mbuzi mumkaka wa mayi ake.+

22 Musamalephere kupereka chakhumi cha zokolola zonse za mʼmunda mwanu chaka ndi chaka.+ 23 Muzidzadya chakhumi cha mbewu zanu, kumwa vinyo wanu watsopano, kudya mafuta anu, ana oyamba a ngʼombe ndi a nkhosa zanu pamaso pa Yehova Mulungu wanu, pamalo amene iye adzasankhe kuikapo dzina lake.+ Muzidzachita zimenezi kuti mudzaphunzire kuopa Yehova Mulungu wanu nthawi zonse.+

24 Koma ngati ulendowo ndi wautali kwa inu ndipo simungathe kunyamula chakhumicho kupita nacho kumalo amene Yehova Mulungu wanu adzasankhe kuikapo dzina lake,+ chifukwa malowo ali kutali ndi inu (chifukwa Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani), 25 muzidzagulitsa chakhumicho ndipo muzidzatenga ndalamazo mʼmanja mwanu nʼkupita kumalo amene Yehova Mulungu wanu adzasankhe. 26 Ndalamazo muzidzagulira chilichonse chimene mtima wanu wafuna, kaya ndi ngʼombe, nkhosa, mbuzi, vinyo, chakumwa choledzeretsa ndi chilichonse chimene mtima wanu wafuna. Ndipo muzidzadya zinthuzi pamaso pa Yehova Mulungu wanu nʼkusangalala, inuyo ndi banja lanu.+ 27 Ndipo musaiwale Mlevi amene akukhala mumzinda wanu,+ chifukwa sanapatsidwe gawo kapena cholowa ngati inuyo.+

28 Kumapeto kwa zaka zitatu zilizonse muzidzabweretsa chakhumi cha zokolola zanu zonse mʼchaka chachitatucho, ndipo muzidzachisiya mkati mwa mzinda wanu.+ 29 Ndiyeno Mlevi, amene sanapatsidwe gawo kapena cholowa ngati inuyo, komanso mlendo, mwana wamasiye ndi mkazi wamasiye amene akukhala mumzinda wanu, azibwera kudzadya ndi kukhuta+ kuti Yehova Mulungu wanu akudalitseni pa chilichonse chimene mukuchita.”+

15 “Kumapeto kwa zaka 7 zilizonse muzimasula anthu amene anakongola zinthu zanu.+ 2 Muzichita izi pomasula anthu angongolewo: Munthu aliyense azimasula mnzake amene ali ndi ngongole yake. Asamakakamize mnzake kapena mʼbale wake kuti abweze ngongoleyo, chifukwa chilengezo choti anthu angongole amasuke chaperekedwa potsatira lamulo la Yehova.+ 3 Mlendo mungathe kumukakamiza kuti abweze ngongole,+ koma ngati mʼbale wanu wakongola chinthu chanu chilichonse, musamukakamize kuti achibweze. 4 Pakati panu pasapezeke munthu wosauka, chifukwa Yehova adzakudalitsani ndithu+ mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani kuti likhale cholowa chanu. 5 Adzakudalitsani pokhapokha ngati mutamvera mosamala mawu a Yehova Mulungu wanu ndi kutsatira mokhulupirika malamulo onsewa amene ndikukupatsani lero.+ 6 Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani mogwirizana ndi zimene anakulonjezani ndipo mitundu yambiri idzakongola zinthu zanu,* koma inu simudzafunika kukongola kanthu.+ Mudzalamulira mitundu yambiri koma mitunduyo sidzakulamulirani.+

7 Ngati mmodzi mwa abale anu wasauka pakati panu, mu umodzi mwa mizinda yanu mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani, musamamuumire mtima kapena kumuumitsira dzanja lanu.+ 8 Koma muzithandiza mʼbale wanuyo mowolowa manja,+ ndipo mulimonse mmene zingakhalire, muzimukongoza* chilichonse chimene akufuna kapena chimene akusowa. 9 Samalani kuti musakhale ndi maganizo oipa awa mumtima mwanu akuti, ‘Chaka cha 7 choti anthu angongole amasuke chayandikira,’+ nʼkulephera kuthandiza mʼbale wanu wosaukayo mowolowa manja, osamupatsa chilichonse. Ngati atafuulira Yehova chifukwa cha zimene inuyo mwamuchitira, mudzakhala kuti mwachimwa.+ 10 Muzimupatsa mowolowa manja zimene akufunazo,+ ndipo musamamupatse* zinthuzo monyinyirika. Mukamachita zimenezi, Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani pa chilichonse chimene mukuchita ndi ntchito zanu zonse.+ 11 Mʼdziko lanu mudzapitirizabe kupezeka anthu osauka.+ Nʼchifukwa chake ndikukulamulani kuti, ‘Muzikhala owolowa manja kwa mʼbale wanu wovutika komanso wosauka mʼdziko lanu.’+

12 Ngati mʼbale wanu anagulitsidwa kwa inu, kaya ndi mwamuna kapena mkazi wa Chiheberi, ndipo wakutumikirani zaka 6, mʼchaka cha 7 muzimumasula nʼkumulola kuti achoke.+ 13 Ndipo mukamʼmasula, musamulole kuti achoke chimanjamanja. 14 Muzimupatsa mowolowa manja zina mwa nkhosa zanu, mbewu zochokera pamalo anu opunthira, mafuta ochokera pamalo oyengera ndi vinyo wochokera moponderamo mphesa. Muzimupatsa mogwirizana ndi mmene Yehova Mulungu wanu wakudalitsirani. 15 Muzikumbukira kuti munali akapolo mʼdziko la Iguputo ndipo Yehova Mulungu wanu anakuwombolani. Nʼchifukwa chake lero ndikukulamulani kuti muzichita zinthu zimenezi.

16 Koma kapoloyo akakuuzani kuti, ‘Ine sindikusiyani!’ chifukwa chakuti amakukondani komanso amakonda banja lanu, ndipo pamene amakhala ndi inu amasangalala,+ 17 muzitenga choboolera nʼkuboola khutu lake ali pakhomo, mpaka chobooleracho chigunde chitseko ndipo azikhala kapolo wanu moyo wake wonse. Muzichitanso zimenezi ndi kapolo wanu wamkazi. 18 Musamaone kuti sipanachitike chilungamo ngati kapolo wanu mwamumasula iye nʼkuchoka, chifukwa ntchito imene wakugwirirani kwa zaka 6 ndi yochuluka kuwirikiza kawiri kuposa ya munthu waganyu, ndipo Yehova Mulungu wanu wakudalitsani pa chilichonse.

19 Mwana aliyense wamphongo woyamba kubadwa wa ngʼombe kapena wa nkhosa muzimupatula nʼkumupereka kwa Yehova Mulungu wanu.+ Musamagwiritse ntchito iliyonse mwana woyamba kubadwa wa ngʼombe,* kapena kumeta ubweya wa mwana woyamba kubadwa wa nkhosa. 20 Chaka chilichonse inuyo ndi banja lanu muzidzadya mwana woyamba kubadwa wa ngʼombe kapena wa nkhosa pamaso pa Yehova Mulungu wanu, pamalo amene Yehova adzasankhe.+ 21 Koma ngati nyamayo ili ndi vuto, monga kulumala kapena khungu, kapena chilema chilichonse chachikulu, musamaipereke nsembe kwa Yehova Mulungu wanu.+ 22 Muziidyera mumzinda wanu* ngati mmene mumadyera insa ndi mbawala.+ Munthu wodetsedwa komanso munthu woyera nayenso azidya nawo. 23 Koma musamadye magazi ake.+ Muziwathira pansi ngati madzi.”+

16 “Muzikumbukira kuti mwezi wa Abibu* ndi wofunika ndipo muzichita chikondwerero cha Pasika kwa Yehova Mulungu wanu,+ chifukwa mʼmwezi wa Abibu Yehova Mulungu wanu anakutulutsani mu Iguputo usiku.+ 2 Ndipo muzipereka nsembe ya Pasika kwa Yehova Mulungu wanu.+ Muzipereka nkhosa ndi ngʼombe+ pamalo amene Yehova adzasankhe kuikapo dzina lake.+ 3 Musamadye nsembeyo limodzi ndi chilichonse chokhala ndi zofufumitsa.+ Kwa masiku 7 muzidya mkate wopanda zofufumitsa, umene ndi mkate wamasautso, chifukwa munatuluka mofulumira mʼdziko la Iguputo.+ Muzichita zimenezi kuti muzikumbukira tsiku limene munatuluka mʼdziko la Iguputo, masiku onse a moyo wanu.+ 4 Musamapezeke ndi mtanda wa ufa wokanda wokhala ndi zofufumitsa mʼdziko lanu lonse kwa masiku 7.+ Nyama iliyonse imene mwapereka nsembe madzulo, pa tsiku loyamba, isamagone mpaka mʼmawa.+ 5 Simudzaloledwa kupereka nsembe ya Pasika mumzinda wanu uliwonse umene Yehova Mulungu wanu akukupatsani. 6 Koma muzidzapereka nsembe ya Pasikayo pamalo amene Yehova Mulungu wanu adzasankhe kuikapo dzina lake. Muzidzapereka nsembeyo madzulo, dzuwa likangolowa,+ pa nthawi yofanana ndi imene munatuluka mu Iguputo. 7 Muzidzaiwotcha nʼkuidya+ pamalo amene Yehova Mulungu wanu adzasankhe,+ ndipo mʼmawa mwake muzidzabwerera kumatenti anu. 8 Muzidya mkate wopanda zofufumitsa kwa masiku 6, ndipo pa tsiku la 7 muzichitira Yehova Mulungu wanu msonkhano wapadera. Pa tsikuli musamagwire ntchito.+

9 Muziwerenga masabata 7. Muziyamba kuwerenga masabata 7 amenewo kuchokera pa nthawi imene mwayamba kumweta tirigu.+ 10 Ndiyeno muzichitira Yehova Mulungu wanu Chikondwerero cha Masabata,+ popereka nsembe zaufulu zimene mungathe, mogwirizana ndi mmene Yehova Mulungu wanu wakudalitsirani.+ 11 Ndipo muzidzasangalala pamaso pa Yehova Mulungu wanu, inuyo, mwana wanu wamwamuna, mwana wanu wamkazi, kapolo wanu wamwamuna, kapolo wanu wamkazi, Mlevi amene akukhala mumzinda wanu,* mlendo amene akukhala pakati panu, mwana wamasiye ndi mkazi wamasiye, amene ali pakati panu. Muzidzasangalala pamalo amene Yehova Mulungu wanu adzasankhe kuikapo dzina lake.+ 12 Muzikumbukira kuti munali akapolo ku Iguputo,+ ndipo muzisunga komanso kutsatira malamulo amenewa.

13 Muzichita Chikondwerero cha Misasa+ kwa masiku 7, mukamatuta zokolola kuchokera pamalo opunthira mbewu, pamalo oyengera mafuta ndi pamalo opondera mphesa. 14 Muzisangalala pa chikondwerero chimenecho,+ inuyo, mwana wanu wamwamuna, mwana wanu wamkazi, kapolo wanu wamwamuna, kapolo wanu wamkazi, Mlevi, mlendo amene akukhala pakati panu, mwana wamasiye ndi mkazi wamasiye, amene ali mumzinda wanu. 15 Muzichitira Yehova Mulungu wanu chikondwerero chimenecho kwa masiku 7+ pamalo amene Yehova adzasankhe. Muzichita chikondwererochi chifukwa Yehova Mulungu wanu adzadalitsa zokolola zanu zonse ndi chilichonse chimene dzanja lanu likuchita,+ ndipo inu mudzakhala osangalala kwambiri.+

16 Mwamuna aliyense pakati panu azikaonekera katatu pa chaka pamaso pa Yehova Mulungu wanu, pamalo amene Mulungu adzasankhe. Azikaonekera pa Chikondwerero cha Mkate Wopanda Zofufumitsa,+ Chikondwerero cha Masabata+ ndi pa Chikondwerero cha Misasa.+ Palibe aliyense wa iwo amene akuyenera kukaonekera kwa Yehova chimanjamanja. 17 Mphatso imene aliyense ayenera kubweretsa izikhala yogwirizana ndi madalitso amene Yehova Mulungu wanu wakupatsani.+

18 Musankhe oweruza+ ndi atsogoleri a fuko lililonse mʼmizinda yonse imene* Yehova Mulungu wanu akukupatsani ndipo aziweruza anthu mwachilungamo. 19 Musamakhotetse chilungamo,+ musamakondere+ kapena kulandira chiphuphu, chifukwa chiphuphu chimachititsa khungu maso a anthu anzeru+ komanso kupotoza mawu a anthu olungama. 20 Muzichita zinthu mwachilungamo+ kuti mukhale ndi moyo nʼkukatenga dziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani.

21 Musadzadzale mtengo uliwonse kuti ukhale mzati wopatulika*+ pafupi ndi guwa lansembe la Yehova Mulungu wanu limene mudzapange.

22 Ndipo musadzaimike chipilala chopatulika,+ chinthu chimene Yehova Mulungu wanu amadana nacho.”

17 “Musamapereke kwa Yehova Mulungu wanu nsembe ya ngʼombe kapena nkhosa imene ili ndi chilema kapena vuto lililonse, chifukwa idzakhala yonyansa kwa Yehova Mulungu wanu.+

2 Ngati pakati panu papezeka mwamuna kapena mkazi amene akuchita zinthu zoipa pamaso pa Yehova Mulungu wanu, mu umodzi mwa mizinda yanu imene Yehova Mulungu wanu akukupatsani ndipo akuphwanya pangano la Mulungu,+ 3 moti wasochera ndipo amalambira milungu ina nʼkumaigwadira, kapena kugwadira dzuwa, mwezi kapena gulu lonse la zinthu zakuthambo,+ zomwe ine sindinakulamuleni,+ 4 ndiye munthu wina akakuuzani zimenezi kapena mwamva zimene zachitika, muzifufuza nkhaniyo mosamala. Mukatsimikizira kuti ndi zoonadi+ kuti chinthu choipachi chachitika mu Isiraeli, 5 muzitenga mwamuna kapena mkazi amene wachita chinthu choipayo nʼkupita naye kunja kwa mzinda, ndipo muzikamuponya miyala kuti afe.+ 6 Munthuyo aziphedwa ngati pali umboni wa* anthu awiri kapena atatu.+ Asaphedwe ngati munthu mmodzi yekha ndi amene wapereka umboni.+ 7 Dzanja la mbonizo lizikhala loyamba kumuponya miyala kuti afe, ndipo anthu ena onse azibwera pambuyo. Choncho muzichotsa woipayo pakati panu.+

8 Ngati mu umodzi mwa mizinda yanu muli mlandu wovuta kwambiri kuweruza kaya ndi mlandu wokhudza kukhetsa magazi,+ mlandu umene munthu wakasuma, mlandu wokhudza zachiwawa kapena mkangano, muzinyamuka nʼkupita kumalo amene Yehova Mulungu wanu adzasankhe.+ 9 Muzipita kwa Alevi omwe ndi ansembe ndi kwa woweruza+ amene akutumikira mʼmasiku amenewo. Muziwafotokozera nkhaniyo ndipo iwo azikuuzani chigamulo.+ 10 Kenako muzichita mogwirizana ndi chigamulo chimene akuuzani kumalo amene Yehova adzasankhe. Muzionetsetsa kuti mukuchita zonse zimene akulangizani. 11 Muzichita mogwirizana ndi lamulo limene akusonyezani komanso chigamulo chimene akuuzani.+ Musapatukire kudzanja lamanja kapena lamanzere pa chigamulo chimene akupatsani.+ 12 Munthu amene adzachite zinthu modzikuza posamvera wansembe amene akutumikira Yehova Mulungu wanu kapena woweruza, ayenera kufa.+ Muzichotsa woipayo mu Isiraeli.+ 13 Anthu onse adzamva zimenezo nʼkuchita mantha ndipo sadzachitanso zinthu modzikuza.+

14 Mukakalowa mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani nʼkulitenga kukhala lanu ndipo mukukhalamo, ndiye inu nʼkunena kuti, ‘Tisankhe mfumu ngati mitundu ina yonse imene yatizungulira,’+ 15 mudzasankhe mfumu imene Yehova Mulungu wanu adzasankhe.+ Mudzasankhe mfumuyo kuchokera pakati pa abale anu. Simukuloledwa kusankha mlendo amene si mʼbale wanu. 16 Koma iye asakhale ndi mahatchi ambiri+ kapena kuchititsa anthu kuti abwerere ku Iguputo kuti akatenge mahatchi ochuluka+ chifukwa Yehova anakuuzani kuti, ‘Musabwererenso kudzera njira iyi.’ 17 Asakhalenso ndi akazi ambiri kuti mtima wake usapatuke+ komanso asakhale ndi siliva ndi golide wambiri.+ 18 Akakhala pampando wachifumu, ayenera kukopera buku lakelake la Chilamulo ichi, kuchokera mʼbuku limene* Alevi omwe ndi ansembe amasunga.+

19 Buku limeneli azikhala nalo nthawi zonse ndipo aziliwerenga masiku onse a moyo wake,+ kuti aphunzire kuopa Yehova Mulungu wake ndi kusunga mawu onse a Chilamulo ichi, komanso kutsatira malangizo ake.+ 20 Akachita zimenezi sadzadzikweza pamaso pa abale ake, komanso sadzachoka pachilamulo nʼkupatukira kudzanja lamanja kapena lamanzere, kuti iyeyo ndi ana ake apitirize kukhala mafumu mu Isiraeli kwa nthawi yaitali.”

18 “Alevi omwe ndi ansembe, komanso fuko lonse la Levi, sadzapatsidwa gawo kapena cholowa pakati pa Aisiraeli. Iwo azidzadya nsembe zowotcha pamoto zoperekedwa kwa Yehova, zomwe ndi cholowa chake.+ 2 Choncho asamalandire cholowa pakati pa abale awo. Cholowa chawo ndi Yehova, mogwirizana ndi zimene anawauza.

3 Tsopano zinthu zimene ansembe azidzalandira kuchokera kwa anthu ndi izi: Amene akupereka nsembe ya ngʼombe kapena nkhosa, azipereka kwa wansembe mwendo wakutsogolo, nsagwada ndi chifu. 4 Aziperekanso kwa wansembe mbewu zawo zoyambirira kucha, vinyo wawo watsopano, mafuta awo ndi ubweya wa nkhosa zawo umene ameta moyambirira.+ 5 Yehova Mulungu wanu wamusankha pamodzi ndi ana ake, pakati pa mafuko anu onse, kuti atumikire mʼdzina la Yehova nthawi zonse.+

6 Koma Mlevi akatuluka mu umodzi mwa mizinda yanu mu Isiraeli kumene ankakhala,+ ndipo akufuna kupita kumalo amene Yehova wasankha,*+ 7 angathe kumatumikira kumeneko mʼdzina la Yehova Mulungu wake mofanana ndi Alevi onse, omwe ndi abale ake, amene akutumikira kumeneko pamaso pa Yehova.+ 8 Chakudya chimene azikalandira chikakhale chofanana ndi cha ansembe onse,+ kuwonjezera pa zimene walandira atagulitsa cholowa chimene analandira kwa makolo ake.

9 Mukakalowa mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani, musakaphunzire kuchita zinthu zonyansa zimene anthu a mitundu yakumeneko akuchita.+ 10 Pakati panu pasapezeke munthu wowotcha mwana wake pamoto,*+ wolosera,+ aliyense wochita zamatsenga,+ aliyense woombeza,+ wanyanga,+ 11 aliyense wochesula* ena, aliyense wofunsira kwa wolankhula ndi mizimu+ kapena wolosera zamʼtsogolo,+ kapena aliyense wofunsira kwa akufa.+ 12 Chifukwa aliyense wochita zimenezi ndi wonyansa kwa Yehova. Ndipo chifukwa chakuti anthu a mitundu ina akuchita zimenezi, Yehova Mulungu wanu akuwathamangitsa pamaso panu. 13 Mukhale opanda cholakwa pamaso pa Yehova Mulungu wanu.+

14 Mitundu imene mukuilanda dziko inkamvera anthu ochita zamatsenga+ ndi olosera.+ Koma Yehova Mulungu wanu sanakuloleni kuti muzichita zimenezi. 15 Yehova Mulungu wanu adzakupatsani mneneri ngati ine kuchokera pakati pa abale anu, ndipo mudzamumvere mneneri ameneyo.+ 16 Adzakupatsani mneneriyu poyankha zimene munapempha Yehova Mulungu wanu ku Horebe, tsiku limene munasonkhana kuphiri.+ Paja munapempha kuti, ‘Mutilole kuti tisamvenso mawu a Yehova Mulungu wathu kapena kuona moto waukuluwu, kuopera kuti tingafe.’+ 17 Ndiyeno Yehova anandiuza kuti, ‘Zimene anenazo ndi zabwino. 18 Ndidzawapatsa mneneri ngati iwe kuchokera pakati pa abale awo.+ Ndidzaika mawu anga mʼkamwa mwake,+ ndipo adzawauza zonse zimene ndidzamulamule.+ 19 Ndipo munthu amene sadzamvera mawu anga amene iye adzalankhule mʼdzina langa, adzayankha mlandu kwa ine.+

20 Ngati mneneri wina angadzikuze nʼkulankhula mʼdzina langa mawu amene sindinamulamule kuti alankhule, kapena kulankhula mʼdzina la milungu ina, mneneri ameneyo afe ndithu.+ 21 Koma munganene mumtima mwanu kuti: “Tidzadziwa bwanji kuti si Yehova amene walankhula mawuwo?” 22 Mneneri akalankhula mʼdzina la Yehova, koma zimene walankhulazo osachitika kapena kukwaniritsidwa, ndiye kuti si Yehova amene walankhula mawu amenewo. Mneneriyo walankhula mawu amenewo modzikuza ndipo musachite naye mantha.’”

19 “Yehova Mulungu wanu akadzawononga mitundu yamʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani, inu nʼkuwalandadi dzikolo ndi kukhala mʼmizinda yawo komanso mʼnyumba zawo,+ 2 mudzapatule mizinda itatu pakati pa dziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani kuti likhale lanu.+ 3 Mudzagawe mʼzigawo zitatu dziko limene Yehova Mulungu wanu wakupatsani kuti likhale lanu, ndipo mudzalambule misewu yopita kumizindayo kuti aliyense wopha munthu azithawira kumizinda imeneyo.

4 Ndiye zimene zizichitika ndi munthu amene wapha mnzake nʼkuthawira kumeneko kuti akhale ndi moyo ndi izi: Ngati wapha mnzake mwangozi ndipo sankadana naye,+ 5 mwachitsanzo, munthu akapita ndi mnzake kuthengo kukafuna nkhuni, ndipo wakweza dzanja lake kuti adule mtengo ndi nkhwangwa koma nkhwangwayo yaguluka mumpini wake nʼkumenya mnzakeyo mpaka kumupha, amene wapha mnzakeyo azithawira ku umodzi mwa mizinda imeneyi kuti akhale ndi moyo.+ 6 Akapanda kutero, chifukwa chakuti wobwezera magazi+ ndi wokwiya kwambiri,* angathamangitse wopha munthuyo nʼkumupeza kenako nʼkumumpha chifukwa chakuti mtunda wopita kumzindawo unali wautali. Koma wopha mnzake mwangoziyo samayenera kufa chifukwa sankadana ndi mnzakeyo.+ 7 Nʼchifukwa chake ndikukulamulani kuti, ‘Mupatule mizinda itatu.’

8 Yehova Mulungu wanu akadzawonjezera dziko lanu mogwirizana ndi zimene analumbira kwa makolo anu,+ nʼkukupatsani dziko lonse limene analonjeza makolo anu kuti adzawapatsa,+ 9 (ngati mutatsatira mokhulupirika malamulo onsewa amene ndikukupatsani lero, akuti muzikonda Yehova Mulungu wanu komanso kuyenda mʼnjira zake nthawi zonse+) mudzawonjezere mizinda inanso itatu pa mizinda imeneyi.+ 10 Mukamachita zimenezi simudzakhetsa magazi a munthu wosalakwa+ mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani ngati cholowa ndipo simudzakhala ndi mlandu wa magazi.+

11 Koma ngati munthu amadana ndi mnzake+ ndipo wamubisalira panjira nʼkumuvulaza kwambiri mpaka mnzakeyo kufa, iye nʼkuthawira ku umodzi mwa mizinda imeneyi, 12 akulu amumzinda wakwawo azimuitanitsa kuchokera kumeneko nʼkumupereka mʼmanja mwa wobwezera magazi ndipo azimupha.+ 13 Musamamumvere* chisoni ndipo muzichotsa mlandu wa magazi a munthu wosalakwa mu Isiraeli+ kuti zinthu zikuyendereni bwino.

14 Mukadzalandira cholowa mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani kuti likhale lanu musamadzasunthe zizindikiro za malire a mnzanu,+ pamalo amene makolo anu anaika kale malire.

15 Mboni imodzi si yokwanira kutsimikizira kuti munthu wachitadi cholakwa kapena tchimo lililonse.+ Muzitsimikizira nkhaniyo mutamva umboni wochokera kwa* mboni ziwiri kapena zitatu.+ 16 Ngati munthu wakonzera mnzake chiwembu nʼkupereka umboni wonama wakuti waphwanya lamulo,+ 17 anthu awiri amene akukanganawo aziima pamaso pa Yehova, kapena kuti pamaso pa ansembe ndi oweruza amene akuweruza masiku amenewo.+ 18 Oweruzawo azifufuza nkhaniyo mosamala+ ndipo ngati munthu amene anapereka umboniyo wapezeka kuti amanama ndipo waneneza mʼbale wake mlandu wabodza, 19 muzimuchitira zimene amafuna kuti zichitikire mʼbale wakezo,+ ndipo muzichotsa woipayo pakati panu.+ 20 Ena onse adzamva nʼkuchita mantha, ndipo sadzachitanso choipa chilichonse ngati chimenechi pakati panu.+ 21 Musamamve* chisoni.+ Pazikhala moyo kulipira moyo, diso kulipira diso, dzino kulipira dzino, dzanja kulipira dzanja, phazi kulipira phazi.”+

20 “Mukapita kunkhondo kukamenyana ndi adani anu, nʼkuona kuti ali ndi mahatchi, magaleta ankhondo komanso asilikali ochuluka kuposa inu, musachite nawo mantha chifukwa Yehova Mulungu wanu, amene anakutulutsani mʼdziko la Iguputo ali ndi inu.+ 2 Mukatsala pangʼono kuyamba nkhondo, wansembe azifika pafupi nʼkulankhula ndi anthu.+ 3 Iye aziwauza kuti, ‘Tamverani Aisiraeli inu. Mwatsala pangʼono kumenyana ndi adani anu. Mitima yanu isachite mantha. Musaope, kuchita mantha kapena kunjenjemera chifukwa cha iwo, 4 chifukwa Yehova Mulungu wanu akuyenda nanu limodzi kuti akumenyereni nkhondo nʼkukupulumutsani kwa adani anu.’+

5 Atsogoleri nawonso aziuza anthuwo kuti, ‘Kodi pali amene wamanga nyumba yatsopano koma sanaitsegulire? Achoke nʼkubwerera kunyumba yakeyo, kuopera kuti angafe pankhondo, ndipo munthu wina angatsegulire nyumbayo. 6 Kodi pali amene walima munda wa mpesa koma sanayambe kukolola zipatso zake? Achoke nʼkubwerera kunyumba yake, kuopera kuti angafe pankhondo ndipo munthu wina angakolole zipatsozo. 7 Kodi pali amene analonjeza mkazi kuti adzamukwatira koma sanamukwatire? Achoke nʼkubwerera kunyumba yake,+ kuopera kuti angafe pankhondo ndipo mwamuna wina angakwatire mkaziyo.’ 8 Atsogoleriwo afunsenso anthuwo kuti, ‘Kodi pali wamantha komanso wosalimba mtima?+ Abwerere kunyumba yake, kuti asachititse mantha mitima ya abale ake ngati mmene iye wachitira.’*+ 9 Atsogoleriwo akamaliza kulankhula ndi anthu, azisankha akulu a magulu ankhondo oti azitsogolera anthuwo.

10 Mukayandikira mzinda kuti mumenyane nawo, muzilengeza kwa anthu amumzindawo mfundo za mtendere.+ 11 Ngati anthu amumzindawo akuyankhani mwamtendere nʼkukutsegulirani mageti ake, anthu onse opezeka mmenemo azikhala anu kuti azikugwirirani ntchito yaukapolo ndipo azikutumikirani.+ 12 Koma ngati anthuwo akana kuchita nanu mtendere, ndipo akuchita nanu nkhondo, inuyo muzizungulira mzindawo, 13 Yehova Mulungu wanu adzaupereka ndithu mʼmanja mwanu, ndipo zikatero muzipha mwamuna aliyense ndi lupanga. 14 Koma muzitenga akazi, ana aangʼono, ziweto ndi chilichonse chopezeka mumzindawo kuti zikhale zanu,+ ndipo muzidya zimene mwatenga kwa adani anu amene Yehova Mulungu wanu wakupatsani.+

15 Muzichita zimenezi ndi mizinda yonse imene ili kutali kwambiri ndi inu, yomwe sili pakati pa mizinda ya mitundu iyi imene yayandikana nanu. 16 Koma mʼmizinda ya anthu awa, imene Yehova Mulungu wanu akukupatsani monga cholowa, musalole kuti mutsale chamoyo chilichonse.+ 17 Mʼmalomwake, mudzawononge anthu onse. Mudzawononge Ahiti, Aamori, Akanani, Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi,+ mogwirizana ndi zimene Yehova Mulungu wanu anakulamulani. 18 Mukawawononge kuti asakakuphunzitseni kuchita zinthu zonse zonyansa zimene achitira milungu yawo nʼkukuchititsani kuti muchimwire Yehova Mulungu wanu.+

19 Mukazungulira mzinda nʼcholinga choti muulande ndipo mwakhala mukumenyana nawo kwa masiku ambiri, musawononge mitengo yake poidula ndi nkhwangwa. Mukhoza kudya zipatso za mitengoyo, koma simukuyenera kuidula.+ Kodi mtengo wamʼmunda ndi munthu kuti muwuukire? 20 Mungathe kuwononga mtengo wokhawo umene mukuudziwa kuti subereka zipatso zakudya. Mtengo woterowo mungaudule nʼkumangira mpanda wozungulira mzinda wa adani amene akuchita nanu nkhondo, mpaka mzindawo utagwa.”

21 “Ngati mwapeza munthu wakufa pathengo, mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani kuti mulitenge kukhala lanu, ndipo amene wapha munthuyo sakudziwika, 2 akulu ndi oweruza anu+ azipita kukayeza mtunda kuchokera pamene pali munthu wakufayo kukafika kumizinda yonse yozungulira malo amene munthuyo wapezeka. 3 Ndiyeno akulu amumzinda umene uli pafupi ndi pamene papezeka munthu wakufayo, azitenga ngʼombe yaingʼono yaikazi imene sanaigwiritsepo ntchito, imene sinasenzepo goli nʼkukoka chilichonse. 4 Akulu a mumzindawo azitenga ngʼombeyo nʼkupita nayo kuchigwa chimene chili* ndi madzi oyenda. Chigwa chimenechi chikhale choti sichinalimidwepo kapena kudzalidwa mbewu. Akafika kumeneko azipha ngʼombe yaingʼonoyo poithyola khosi.+

5 Ansembe, omwe ndi Alevi, azifika pafupi chifukwa ndi amene Yehova Mulungu wanu wawasankha kuti azimutumikira+ komanso azidalitsa mʼdzina la Yehova.+ Iwo ndi amene akuyenera kunena njira yothetsera mkangano uliwonse wokhudza zinthu zankhanza zimene zachitika.+ 6 Ndiyeno akulu onse amumzinda umene uli pafupi ndi munthu wakufayo azisamba mʼmanja+ pamwamba pa ngʼombe imene yathyoledwa khosi mʼchigwa ija. 7 Ndipo iwo azinena kuti, ‘Manja athu sanakhetse magazi awa, ndiponso maso athu sanaone magaziwa akukhetsedwa. 8 Inu Yehova, musaimbe mlanduwu anthu anu Aisiraeli amene munawawombola,+ ndipo musalole kuti mlandu wa magazi a munthu wosalakwa ukhale pa anthu anu Aisiraeli.’+ Akatero iwo sadzaimbidwa mlandu wa magaziwo. 9 Mukadzachita zimenezi mudzachotsa mlandu wa magazi a munthu wosalakwa pakati panu, chifukwa mudzakhala mutachita zinthu zoyenera pamaso pa Yehova.

10 Mukapita kunkhondo kukamenyana ndi adani anu, ndipo Yehova Mulungu wanu wakugonjetserani adaniwo, inu nʼkuwatenga kuti akhale akapolo,+ 11 ndipo pakati pa anthu ogwidwawo mwaonapo mkazi wokongola ndipo mwakopeka naye moti mukufuna kumutenga kuti akhale mkazi wanu, 12 mungathe kumutenga nʼkulowa naye mʼnyumba yanu. Kenako azimeta tsitsi lake nʼkusamalira zikhadabo zake. 13 Azisintha zovala zimene anavala pa nthawi imene ankagwidwa ukapolo ndipo azikhala mʼnyumba mwanu. Azilira maliro a bambo ake ndi a mayi ake kwa mwezi wathunthu,+ kenako mungathe kugona naye. Inu mudzakhala mwamuna wake ndipo iye adzakhala mkazi wanu. 14 Koma ngati simukusangalala naye muzimulola kuti achoke+ nʼkupita kulikonse kumene akufuna. Koma simukuyenera kumugulitsa kapena kumuchitira nkhanza, chifukwa mwamuchititsa manyazi.

15 Ngati mwamuna ali ndi akazi awiri, koma amakonda mmodzi kuposa winayo,* ndipo akazi onsewo anamuberekera ana aamuna, koma mwana woyamba kubadwa ndi wa mkazi wosakondedwayo,+ 16 pa tsiku limene adzagawe cholowa kwa ana ake aamuna, sadzaloledwa kutenga mwana wamwamuna wa mkazi wokondedwa uja ngati mwana wake woyamba kubadwa mʼmalo mwa mwana wamwamuna wa mkazi wosakondedwayo, amene ndi woyamba kubadwa. 17 Azivomereza kuti mwana wamwamuna wa mkazi wake wosakondedwayo ndiye woyamba kubadwa, pomupatsa magawo awiri pa chilichonse chimene ali nacho chifukwa iye ndi chiyambi cha mphamvu zake zobereka. Mwana ameneyo ndi amene ali woyenera kulandira udindo wa mwana woyamba kubadwa.+

18 Ngati munthu ali ndi mwana wamwamuna wosamvera komanso wopanduka, amene samvera bambo ake kapena mayi ake,+ ndipo ayesetsa kumulangiza koma amakana kuwamvera,+ 19 bambo ake ndi mayi ake azimugwira nʼkupita naye kwa akulu kugeti la mzinda wawo, 20 ndipo aziuza akulu amzindawo kuti, ‘Mwana wathuyu ndi wosamva komanso ndi wopanduka ndipo amakana kutimvera. Ndi wosusuka+ komanso ndi chidakwa.’+ 21 Kenako amuna onse a mumzinda wawo azimuponya miyala nʼkumupha. Choncho muzichotsa woipayo pakati panu, ndipo Aisiraeli onse adzamva nʼkuchita mantha.+

22 Ngati munthu wachita tchimo loyenera chiweruzo choti aphedwe,+ ndiyeno munthuyo waphedwa, ndipo mwamupachika pamtengo,+ 23 mtembo wake usamakhale pamtengopo usiku wonse.+ Mʼmalomwake, muzionetsetsa kuti mwamuika mʼmanda tsiku lomwelo, chifukwa munthu aliyense wopachikidwa pamtengo ndi wotembereredwa ndi Mulungu.+ Musamaipitse dziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani kuti likhale cholowa chanu.”+

22 “Mukaona ngʼombe kapena nkhosa ya mʼbale wanu ikusochera, musamangoisiya osaibweza.+ Muziikusa nʼkuipititsa kwa mʼbale wanuyo. 2 Koma ngati mwiniwake sakhala pafupi ndi inu kapena simukumudziwa, muzitenga chiwetocho nʼkupita nacho kunyumba kwanu. Muzisunga chiwetocho mpaka mwiniwakeyo atafika kudzachifufuza ndipo muzimubwezera.+ 3 Muzichita zimenezi ndi bulu wa mʼbale wanu, nsalu yake, kapena chilichonse chimene mʼbale wanu wataya inu nʼkuchipeza. Simukuyenera kungochisiya osachitola.

4 Mukaona bulu wa mʼbale wanu kapena ngʼombe yake itagwa pamsewu musamangoisiya. Muzimuthandiza mʼbale wanuyo poidzutsa.+

5 Mkazi asamavale chovala cha mwamuna ndipo mwamuna asamavale chovala cha mkazi. Chifukwa aliyense wochita zimenezi ndi wonyansa kwa Yehova Mulungu wanu.

6 Ngati mwapeza chisa cha mbalame mʼmbali mwa msewu kaya chili mumtengo kapena pansi, muli ana kapena mazira, mayi atafungatira ana kapena mazirawo, musamatenge mayi ndi ana omwe.+ 7 Muzionetsetsa kuti mwathamangitsa mayiyo, koma anawo mungathe kuwatenga. Muzichita zimenezi kuti zinthu zikuyendereni bwino komanso kuti mukhale ndi moyo nthawi yaitali.

8 Mukamanga nyumba yatsopano muzimanganso kampanda padenga la nyumbayo+ kuopera kuti nyumba yanu ingakhale ndi mlandu wa magazi ngati munthu atagwa kuchokera padengapo.

9 Mʼmunda wanu wa mpesa musamadzalemo mbewu zamitundu ina,+ chifukwa mukachita zimenezo zokolola zanu zonse komanso mphesa zanu zidzaperekedwa kumalo opatulika.

10 Musamamange ngʼombe ndi bulu kuti muzilimitse pamodzi.+

11 Musamavale chovala chimene anachipanga pophatikiza ubweya wa nkhosa ndi ulusi wa thonje.+

12 Muzimanga ulusi mʼmakona 4 a chovala chanu.+

13 Mwamuna akatenga mkazi nʼkugona naye koma sakumukondanso,* 14 ndipo akumuimba mlandu wochita khalidwe loipa komanso wamuipitsira mbiri yake ponena kuti: ‘Ine ndinatenga mkazi uyu koma nditagona naye, sindinapeze umboni uliwonse woti anali namwali.’ 15 Zikatero bambo ndi mayi a mtsikanayo azipititsa umboni wosonyeza kuti mtsikanayo anali namwali kwa akulu a mzinda, kugeti la mzindawo. 16 Bambo a mtsikanayo aziuza akuluwo kuti, ‘Ine ndinapereka mwana wanga wamkazi kwa mwamuna uyu kuti akhale mkazi wake koma akudana naye,* 17 ndipo akumuimba mlandu wochita khalidwe loipa ponena kuti: “Ndaona kuti palibe umboni wosonyeza kuti mwana wanuyu anali namwali.” Koma umboni wosonyeza kuti mwana wanga anali namwali ndi uwu.’ Akatero azitambasula chofunda pamaso pa akulu a mzindawo. 18 Ndiyeno akulu+ a mzindawo azigwira mwamunayo nʼkumupatsa chilango.+ 19 Akatero azimulipiritsa masekeli* 100 asiliva, ndipo azipereka ndalamazo kwa bambo a mtsikanayo chifukwa waipitsa mbiri ya namwali wa mu Isiraeli.+ Mtsikanayo apitirize kukhala mkazi wake ndipo sadzaloledwa kumusiya masiku onse a moyo wake.

20 Koma ngati zatsimikizika kuti ndi zoona ndipo palibe umboni wosonyeza kuti mtsikanayo anali namwali, 21 azibweretsa mtsikanayo pakhomo la nyumba ya bambo ake ndipo amuna amumzindawo azimuponya miyala kuti afe, chifukwa wachita chinthu chochititsa manyazi mu Isiraeli,+ pochita chiwerewere* mʼnyumba ya bambo ake.+ Choncho muzichotsa woipayo pakati panu.+

22 Ngati mwamuna wapezeka akugona ndi mkazi wa mwiniwake, onse awiri, mwamuna amene amagona ndi mkaziyo komanso mkaziyo, azifera limodzi.+ Choncho muzichotsa oipawo mu Isiraeli.

23 Ngati namwali analonjezedwa ndi mwamuna kuti adzamukwatira, ndipo mwamuna wina wamupeza mumzinda nʼkugona naye, 24 onse awiri muziwapititsa kugeti la mzindawo nʼkuwaponya miyala kuti afe. Mtsikanayo afe chifukwa chakuti sanakuwe mumzindawo ndipo mwamunayo afe chifukwa waipitsa mkazi wa mnzake.+ Choncho muzichotsa oipawo pakati panu.

25 Koma ngati mwamunayo anapeza mtsikana wolonjezedwa kukwatiwayo kuthengo nʼkumugwiririra, mwamunayo afe yekha. 26 Mtsikanayo musamuchite chilichonse. Iye sanachite tchimo loyenera imfa. Mlanduwu ukufanana ndi wa munthu amene waukira mnzake nʼkumupha.+ 27 Chifukwa chakuti anamupeza kuthengo, ndipo mtsikanayo anakuwa koma panalibe womupulumutsa.

28 Ngati mwamuna wakumana ndi namwali amene sanalonjezedwe ndi mwamuna kuti adzamukwatira ndipo wamugwira nʼkugona naye, ndiyeno agwidwa,+ 29 mwamunayo azipereka masekeli 50 asiliva kwa bambo a mtsikanayo, ndipo azikhala mkazi wake.+ Chifukwa chakuti wamuchititsa manyazi, sadzaloledwa kumusiya masiku onse a moyo wake.

30 Pasapezeke mwamuna aliyense wokwatira mkazi wa bambo ake kuti asachititse manyazi bambo akewo.”*+

23 “Mwamuna amene anafulidwa pophwanya mavalo ake kapena amene anadulidwa maliseche asamalowe mumpingo wa Yehova.+

2 Mwana wapathengo asamalowe mumpingo wa Yehova.+ Ngakhale mpaka mʼbadwo wa 10, mbadwa zake zisamalowe mumpingo wa Yehova.

3 Mbadwa ya Amoni kapena Mowabu isamalowe mumpingo wa Yehova.+ Ngakhale mpaka mʼbadwo wa 10, mbadwa zawo zisadzalowe mumpingo wa Yehova mpaka kalekale, 4 chifukwa chakuti sanakuthandizeni pokupatsani chakudya ndi madzi pamene munali pa ulendo mutatuluka mu Iguputo,+ komanso chifukwa chakuti analemba ganyu Balamu mwana wa Beori, amene kwawo ndi ku Petori ku Mesopotamiya kuti akutemberereni.+ 5 Koma Yehova Mulungu wanu anakana kumvera Balamu.+ Mʼmalomwake, Yehova Mulungu wanu anakusinthirani temberero kukhala dalitso,+ chifukwa Yehova Mulungu wanu anakukondani.+ 6 Musamachite chilichonse powathandiza kuti azikhala mwamtendere komanso kuti zinthu ziwayendere bwino masiku onse a moyo wanu.+

7 Musamadane ndi mbadwa ya Edomu, chifukwa ndi mʼbale wanu.+

Musamadane ndi munthu wa ku Iguputo, chifukwa munali alendo mʼdziko lawo.+ 8 Ana awo a mʼbadwo wachitatu angathe kulowa mumpingo wa Yehova.

9 Mukamanga msasa kuti mumenyane ndi adani anu, muzipewa chilichonse chodetsa.*+ 10 Ngati mwamuna wadetsedwa chifukwa chotulutsa umuna usiku,+ azipita kunja kwa msasa ndipo asamalowenso mumsasamo. 11 Ndiyeno madzulo azisamba ndi madzi ndipo kenako angathe kubwerera kumsasa dzuwa likalowa.+ 12 Muzikhala ndi malo apadera* kunja kwa msasa, kumene muzipita mukafuna kudzithandiza. 13 Pa zida zanu pazikhalanso chokumbira. Ndiyeno mukafuna kudzithandiza kunja kwa msasa, muzikumba dzenje ndi chokumbiracho ndipo mukamaliza muzikwirira zoipazo. 14 Chifukwa Yehova Mulungu wanu akuyendayenda mumsasa wanu+ kuti akupulumutseni ndi kupereka adani anu mʼmanja mwanu. Choncho msasa wanu uzikhala woyera,+ kuti asaone choipa chilichonse pakati panu nʼkusiya kuyenda nanu limodzi.

15 Kapolo akathawa kwa mbuye wake nʼkubwera kwa inu, musamamubweze kwa mbuye wakeyo. 16 Iye azikhala pakati panu pamalo alionse amene angasankhe mu umodzi mwa mizinda yanu, kulikonse kumene wakonda. Ndipo musamamuzunze.+

17 Mwana wamkazi aliyense wa Chiisiraeli asakhale hule wapakachisi,+ ndiponso mwana wamwamuna aliyense wa Chiisiraeli asakhale hule wapakachisi.+ 18 Musamabweretse malipiro a hule lalikazi kapena malipiro a hule lalimuna* mʼnyumba ya Yehova Mulungu wanu kuti mukwaniritse lonjezo lililonse, chifukwa malipiro onsewo ndi onyansa kwa Yehova Mulungu wanu.

19 Mʼbale wanu musamamulipiritse chiwongoladzanja pa ndalama,+ chakudya kapena pa chilichonse chimene munthu angafunepo chiwongoladzanja. 20 Mlendo mungamulipiritse chiwongoladzanja,+ koma mʼbale wanu musamamulipiritse chiwongoladzanja,+ kuti Yehova Mulungu wanu akudalitseni pa chilichonse chimene mukuchita mʼdziko limene mukupita kukalitenga kuti likhale lanu.+

21 Mukalonjeza kanthu kwa Yehova Mulungu wanu+ musamachedwe kukwaniritsa zimene mwalonjezazo.+ Chifukwa Yehova Mulungu wanu adzafuna ndithu kuti mukwaniritse zimene mwalonjezazo. Mukapanda kutero mudzakhala kuti mwachimwa.+ 22 Koma mukapanda kulonjeza, simudzachimwa.+ 23 Muzisunga mawu a pakamwa panu+ ndipo muzikwaniritsa zimene munalonjeza ndi pakamwa panu monga nsembe yaufulu yoperekedwa kwa Yehova Mulungu wanu.+

24 Mukalowa mʼmunda wa mpesa wa mnzanu mungathe kudya mphesa mmene mungathere kuti mukhute, koma musamaike zina mʼthumba lanu.+

25 Mukalowa mʼmunda wa tirigu wa mnzanu, mungathe kupulula ndi dzanja lanu tirigu amene wacha, koma musamamwete ndi chikwakwa tirigu wa mnzanu.”+

24 “Ngati mwamuna wakwatira mkazi koma mkaziyo sakumusangalatsa chifukwa wamupeza ndi vuto linalake, azimulembera kalata yothetsera ukwati+ nʼkumupatsa, ndipo azimuchotsa panyumba pake.+ 2 Akachoka panyumba ya mwamunayo, angathe kupita kukakhala mkazi wa mwamuna wina.+ 3 Ngati mwamuna wachiwiriyo wadana naye* mkaziyo ndipo wamulembera kalata yothetsera ukwati nʼkumupatsa kenako nʼkumuthamangitsa panyumba pake, kapena ngati mwamuna wachiwiriyo, amene anakwatira mkaziyo wamwalira, 4 mwamuna woyamba amene anamuthamangitsa uja sadzaloledwa kumutenganso kuti akhale mkazi wake pambuyo poti waipitsidwa, chifukwa zimenezo ndi zonyansa kwa Yehova. Musamachite machimo amenewa mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani kuti likhale cholowa.

5 Mwamuna akakwatira kumene, asamakhale mʼgulu lankhondo, ndiponso asamapatsidwe ntchito iliyonse. Azikhala kunyumba kwa chaka chimodzi osachita zinthu zimenezi kuti asangalatse mkazi wake.+

6 Munthu asamalande mnzake mphero kapena mwala waungʼono woperera ngati chikole cha ngongole,+ chifukwa kutenga zinthu zimenezi kuli ngati kutenga moyo wa munthu ngati chikole.

7 Munthu akapezeka ataba mmodzi mwa abale ake, Aisiraeli, ndipo wamuchitira nkhanza nʼkumugulitsa,+ wakuba munthuyo ayenera kufa.+ Muzichotsa woipayo pakati panu.+

8 Ngati kwabuka matenda a khate,* muzionetsetsa kuti mukuchita zinthu zonse mogwirizana ndi zimene Alevi omwe ndi ansembe akulangizani.+ Muzionetsetsa kuti mukuchita mogwirizana ndi zimene ndinawalamula. 9 Muzikumbukira zimene Yehova Mulungu wanu anachitira Miriamu panjira mutatuluka mʼdziko la Iguputo.+

10 Ngati mwapereka ngongole ya mtundu uliwonse kwa mnzanu,+ musamalowe mʼnyumba yake kukatenga chimene wanena kuti akupatsani kuti chikhale chikole. 11 Muziima panja, ndipo munthu amene munamupatsa ngongoleyo azikubweretserani yekha chikolecho panjapo. 12 Ndipo ngati munthuyo ndi wosauka, musamagone ndi chinthu chake chimene wakupatsani kuti chikhale chikolecho.+ 13 Muzionetsetsa kuti mwamubwezera chikolecho dzuwa likangolowa, kuti azipita kukagona ali ndi chofunda chake.+ Mukatero iye adzakudalitsani, ndipo mudzakhala mutachita chilungamo pamaso pa Yehova Mulungu wanu.

14 Musamabere mwachinyengo waganyu yemwe ndi wovutika ndiponso wosauka, kaya akhale mmodzi wa abale anu kapena mlendo amene akukhala mʼdziko lanu, amene ali mʼmizinda yanu.*+ 15 Muzimupatsa malipiro ake tsiku lomwelo dzuwa lisanalowe,+ chifukwa iye ndi wosauka ndipo akudalira malipiro ake omwewo kuti akhale ndi moyo. Mukapanda kutero adzafuula kwa Yehova chifukwa cha zimene inuyo mwamuchitira ndipo mudzapezeka kuti mwachimwa.+

16 Abambo asamaphedwe chifukwa cha zimene ana awo achita, ndipo ana asamaphedwe chifukwa cha zimene abambo awo achita.+ Munthu aliyense aziphedwa chifukwa cha tchimo lake.+

17 Musamapotoze chiweruzo cha mlandu wa mlendo kapena mlandu wa mwana wamasiye,+ ndipo musamalande chovala cha mkazi wamasiye kuti chikhale chikole.+ 18 Muzikumbukira kuti munali akapolo mʼdziko la Iguputo, ndipo Yehova Mulungu wanu anakuwombolani kumeneko.+ Nʼchifukwa chake ndikukulamulani kuti muzichita zimenezi.

19 Mukaiwala mtolo wa tirigu pokolola mʼmunda mwanu, musamabwerere kukatenga mtolowo. Muzisiyira mlendo wokhala mʼdziko lanu, mwana wamasiye ndi mkazi wamasiye.+ Muzichita zimenezi kuti Yehova Mulungu wanu akudalitseni pa chilichonse chimene mukuchita.+

20 Mukamakwapula mitengo ya maolivi pokolola, musamabwereze kukwapula nthambi zimene mwakwapula kale. Zimene zatsala zizikhala za mlendo wokhala mʼdziko lanu, mwana wamasiye ndi mkazi wamasiye.+

21 Mukamakolola mphesa mʼmunda wanu, musamabwerere kukakunkha zotsala. Mphesa zotsalazo zizikhala za mlendo wokhala mʼdziko lanu, mwana wamasiye ndi mkazi wamasiye. 22 Muzikumbukira kuti munali akapolo mʼdziko la Iguputo. Nʼchifukwa chake ndikukulamulani kuti muzichita zimenezi.”

25 “Amuna akakangana azipita kwa oweruza,+ oweruzawo azigamula mlanduwo. Wolungama azimuweruza kuti alibe mlandu ndipo woipa azimuweruza kuti ali ndi mlandu.+ 2 Ngati woipayo akuyenera kukwapulidwa,+ woweruza azilamula kuti woipayo amugoneke pansi, ndipo azimukwapula pamaso pa woweruzayo. Azimukwapula zikwapu zogwirizana ndi choipa chimene wachita. 3 Akhoza kumukwapula mpaka zikwapu zokwana 40+ koma zisapitirire pamenepo. Ngati atapitiriza kumukwapula zikwapu zina kuwonjezera pamenepa, mʼbale wakoyo angachititsidwe manyazi pamaso pako.

4 Usamange ngʼombe pakamwa pamene ikupuntha mbewu.”+

5 Ngati amuna apachibale akukhala moyandikana, ndiyeno mmodzi nʼkumwalira asanabereke mwana wamwamuna, mkazi wa womwalirayo asakwatiwe ndi mwamuna wochokera mʼbanja lina. Mlamu wake azipita kwa iye nʼkukamutenga kukhala mkazi wake, ndipo azichita ukwati wa pachilamu.+ 6 Mwana woyamba amene mkaziyo angabereke, azitenga dzina la mwamuna womwalira uja,+ kuti dzina la mʼbale wake lisathe mu Isiraeli.+

7 Ndiye ngati mwamunayo sakufuna kukwatira mkazi wamasiye wa mchimwene wakeyo, mkaziyo azipita kwa akulu pageti nʼkuwauza kuti, ‘Mchimwene wa mwamuna wanga wakana kusunga dzina la mchimwene wake mu Isiraeli. Sanavomereze kuchita ukwati wa pachilamu ndi ine.’ 8 Akulu a mzindawo azimuitana nʼkulankhula naye. Iye akapitiriza kukana nʼkunena kuti, ‘Sindikufuna kukwatira mkazi ameneyu,’ 9 mkazi wamasiyeyo aziyandikira mchimwene wa mwamuna wakeyo akuluwo akuona ndipo azimuvula nsapato+ nʼkumulavulira kumaso nʼkunena kuti, ‘Izi nʼzimene ziyenera kuchitikira munthu amene wakana kumanga nyumba ya mchimwene wake.’ 10 Ndiyeno dzina la banja lake* mu Isiraeli lizidziwika kuti, ‘Nyumba ya amene anavulidwa nsapato uja.’

11 Ngati amuna akumenyana ndipo mkazi wa mmodzi mwa amunawo wabwera kudzalanditsa mwamuna wake mʼmanja mwa amene akumumenya, ndipo mkaziyo watambasula dzanja nʼkugwira maliseche a mwamuna winayo, 12 muzidula dzanja la mkaziyo, ndipo musamumvere chisoni.*

13 Mʼthumba lanu musamakhale miyezo iwiri yosiyana yoyezera kulemera kwa chinthu,+ musamakhale ndi muyezo waukulu ndi wina waungʼono. 14 Mʼnyumba mwanu musamakhale zoyezera ziwiri zosiyana,*+ musamakhale ndi muyezo waukulu komanso muyezo waungʼono. 15 Muzikhala ndi muyezo wolondola ndi woyenera woyezera kulemera kwa chinthu komanso muyezo wolondola ndi woyenera woyezera kuchuluka kwa zinthu, kuti masiku anu achuluke mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani.+ 16 Chifukwa munthu aliyense wopanda chilungamo amene amachita zimenezi ndi wonyansa kwa Yehova Mulungu wanu.+

17 Muzikumbukira zimene Aamaleki anakuchitirani panjira pamene munkachoka ku Iguputo.+ 18 Iwo anakumana nanu panjira nʼkupha anthu onse amene ankayenda movutika kumbuyo kwanu. Iwo anachita izi pamene munali olefuka ndi otopa ndipo sanaope Mulungu. 19 Ndiye Yehova Mulungu wanu akadzakupumitsani kwa adani anu onse okuzungulirani, mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani kuti mulitenge kukhala cholowa chanu,+ mudzafafanize dzina la Aamaleki pansi pa thambo.+ Musadzaiwale zimenezi.

26 “Mukakalowa mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani kuti likhale cholowa chanu, ndipo mukakalitengadi nʼkumakhalamo, 2 mukatenge zina mwa zipatso zoyambirira pa zokolola* zonse zamʼmunda mwanu zimene mudzakolole mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani. Mukaziike mʼdengu nʼkupita nazo kumalo amene Yehova Mulungu wanu adzasankhe kuika dzina lake.+ 3 Muzikapita kwa wansembe amene azidzatumikira masiku amenewo nʼkumuuza kuti, ‘Lero ndikuvomereza pamaso pa Yehova Mulungu wanu kuti ndalowadi mʼdziko limene Yehova analumbira kwa makolo athu kuti adzatipatsa.’+

4 Ndiyeno wansembeyo azikalandira dengulo mʼmanja mwanu nʼkuliika pafupi ndi guwa lansembe la Yehova Mulungu wanu. 5 Kenako muzikanena pamaso pa Yehova Mulungu wanu kuti, ‘Bambo anga anali munthu wongoyendayenda wa Chiaramu*+ ndipo anapita ku Iguputo+ ndi anthu ochepa amʼbanja lawo+ nʼkukakhala kumeneko monga mlendo. Koma ali kumeneko anakhala mtundu waukulu ndi wamphamvu.+ 6 Ndipo Aiguputo anayamba kutizunza komanso kutipondereza, moti ankatigwiritsa ntchito yowawa yaukapolo.+ 7 Choncho tinayamba kufuulira Yehova, Mulungu wa makolo athu, ndipo Yehova anamva mawu athu nʼkuona masautso athu, mavuto athu ndi kuponderezedwa kwathu.+ 8 Pamapeto pake Yehova anatitulutsa mu Iguputo ndi dzanja lamphamvu ndi mkono wotambasula,+ zinthu zochititsa mantha, zizindikiro ndiponso zodabwitsa.+ 9 Ndiyeno anatibweretsa kumalo ano nʼkutipatsa dziko ili, dziko loyenda mkaka ndi uchi.+ 10 Choncho ndabweretsa zipatso zoyambirira mwa zipatso za mʼdziko limene Yehova anandipatsa.’+

Ndipo muzikaziika pamaso pa Yehova Mulungu wanu nʼkugwada pamaso pa Yehova Mulungu wanu. 11 Mukatero muzikasangalala chifukwa cha zabwino zonse zimene Yehova Mulungu wanu wapereka kwa inuyo ndi anthu a mʼnyumba yanu, komanso kwa Mlevi ndi mlendo amene akukhala pakati panu.+

12 Mukamaliza kusonkhanitsa chakhumi+ chonse cha zokolola zanu mʼchaka chachitatu, chaka chopereka chakhumi, muzikapereka chakhumicho kwa Mlevi, mlendo amene akukhala pakati panu, mwana wamasiye ndi mkazi wamasiye ndipo azidzadya nʼkukhuta mʼmizinda yanu.*+ 13 Kenako muzidzanena pamaso pa Yehova Mulungu wanu kuti, ‘Ndachotsa zinthu zonse zopatulika mʼnyumba mwanga nʼkuzipereka kwa Mlevi, mlendo amene akukhala pakati pathu, mwana wamasiye ndi mkazi wamasiye,+ mogwirizana ndi zimene munandilamula. Sindinaphwanye kapena kunyalanyaza malamulo anu. 14 Sindinadyeko zina mwa zimenezi pa nthawi imene ndinali pa chisoni,* kapena kutengapo zina mwa zimenezi ndili wodetsedwa, kapena kupereka zina mwa zinthu zimenezi chifukwa cha munthu wakufa. Ndamvera mawu a Yehova Mulungu wanga ndipo ndachita zonse zimene munandilamula. 15 Tsopano yangʼanani pansi kuchokera kumwamba, kumalo anu oyera okhalako, ndipo mudalitse anthu anu Aisiraeli ndi dziko limene mwatipatsa,+ dziko loyenda mkaka ndi uchi,+ mogwirizana ndi zimene munalumbira kwa makolo athu.’+

16 Lero Yehova Mulungu wanu akukulamulani kuti muzitsatira malangizo ndi zigamulo zimenezi. Choncho muzisunga ndi kutsatira zimenezi ndi mtima wanu wonse+ komanso moyo wanu wonse. 17 Lero Yehova wakutsimikizirani kuti adzakhala Mulungu wanu ngati mukuyenda mʼnjira zake ndi kusunga malangizo ake,+ malamulo ake+ ndi zigamulo zake+ ndiponso ngati mukumvera mawu ake. 18 Ndipo lero mwatsimikizira Yehova kuti mudzakhala anthu ake komanso chuma chake chapadera,+ mogwirizana ndi zimene anakulonjezani. Ndiponso mwamutsimikizira kuti mudzasunga malamulo ake onse. 19 Zikadzatero adzakukwezani pamwamba pa mitundu ina yonse imene anapanga.+ Zimenezi zidzachititsa kuti mutamandidwe, mutchuke komanso kuti mulandire ulemerero mukapitiriza kukhala anthu oyera kwa Yehova Mulungu wanu,+ mogwirizana ndi zimene anakulonjezani.”

27 Ndiyeno Mose pamodzi ndi akulu a Isiraeli analamula anthuwo kuti: “Muzisunga lamulo lililonse limene ndikukupatsani lero. 2 Ndipo tsiku limene muwoloke Yorodano nʼkulowa mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani, mukaimike miyala ikuluikulu nʼkuipanga pulasitala.*+ 3 Kenako mukakawoloka, mukalembe pamiyalapo mawu onse a mʼChilamulo ichi, kuti mulowe mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani, dziko loyenda mkaka ndi uchi, mogwirizana ndi zimene Yehova, Mulungu wa makolo anu anakulonjezani.+ 4 Mukawoloka Yorodano, mukaimike miyala imeneyi paphiri la Ebala,+ ndipo mukaipange pulasitala,* mogwirizana ndi zimene ndikukulamulani lero. 5 Komanso mukamangire Yehova Mulungu wanu guwa lansembe kumeneko, guwa lansembe lamiyala. Musakaseme miyalayo ndi chipangizo chilichonse chachitsulo.+ 6 Mukagwiritse ntchito miyala yathunthu pomangira Yehova Mulungu wanu guwa lansembe, ndipo mukapereke nsembe zopsereza kwa Yehova Mulungu wanu paguwalo. 7 Mukapereke nsembe zamgwirizano+ nʼkuzidyera pamenepo,+ ndipo mukasangalale pamaso pa Yehova Mulungu wanu.+ 8 Ndipo mukalembe moonekera bwino pamiyalayo mawu onse a mʼChilamulo chimenechi.”+

9 Kenako Mose komanso ansembe omwe ndi Alevi analankhula ndi Aisiraeli onse kuti: “Aisiraeli inu, khalani chete ndi kumvetsera. Lero mwakhala anthu a Yehova Mulungu wanu.+ 10 Muzimvera mawu a Yehova Mulungu wanu ndi kusunga malamulo+ ndi malangizo ake, amene ndikukupatsani lero.”

11 Tsiku limenelo Mose analamula anthuwo kuti: 12 “Mukawoloka Yorodano, mafuko otsatirawa ndi amene adzaimirire paphiri la Gerizimu+ nʼkudalitsa anthu: Fuko la Simiyoni, Levi, Yuda, Isakara, Yosefe ndi Benjamini. 13 Ndipo mafuko otsatirawa ndi amene adzaimirire paphiri la Ebala+ kuti azidzavomereza matemberero akamadzatchulidwa: Fuko la Rubeni, Gadi, Aseri, Zebuloni, Dani ndi Nafitali. 14 Ndipo Alevi azidzalankhula mokweza kwa anthu onse a mu Isiraeli kuti:+

15 ‘Wotembereredwa ndi munthu aliyense wopanga chifaniziro chosema+ kapena chifaniziro chachitsulo+ nʼkuchibisa.* Chifanizirocho, chomwe ndi ntchito ya manja a mmisiri waluso,* ndi chonyansa kwa Yehova.’+ (Anthu onse azidzayankha kuti, ‘Zikhale momwemo!’*)

16 ‘Wotembereredwa ndi munthu wonyoza bambo ake kapena mayi ake.’+ (Anthu onse azidzayankha kuti, ‘Zikhale momwemo!’)

17 ‘Wotembereredwa ndi munthu wosuntha chizindikiro cha malire a mnzake.’+ (Anthu onse azidzayankha kuti, ‘Zikhale momwemo!’)

18 ‘Wotembereredwa ndi munthu wosocheretsa munthu amene ali ndi vuto losaona.’+ (Anthu onse azidzayankha kuti, ‘Zikhale momwemo!’)

19 ‘Wotembereredwa ndi munthu wopotoza chiweruzo cha mlendo+ amene akukhala pakati panu, mwana wamasiye ndi mkazi wamasiye.’+ (Anthu onse azidzayankha kuti, ‘Zikhale momwemo!’)

20 ‘Wotembereredwa ndi munthu wogona ndi mkazi wa bambo ake, chifukwa wachititsa manyazi bambo akewo.’*+ (Anthu onse azidzayankha kuti, ‘Zikhale momwemo!’)

21 ‘Wotembereredwa ndi munthu wogona ndi nyama iliyonse.’+ (Anthu onse azidzayankha kuti, ‘Zikhale momwemo!’)

22 ‘Wotembereredwa ndi munthu wogona ndi mchemwali wake, mwana wamkazi wa bambo ake kapena mwana wamkazi wa mayi ake.’+ (Anthu onse azidzayankha kuti, ‘Zikhale momwemo!’)

23 ‘Wotembereredwa ndi mwamuna wogona ndi apongozi ake.’+ (Anthu onse azidzayankha kuti, ‘Zikhale momwemo!’)

24 ‘Wotembereredwa ndi munthu wobisalira mnzake nʼkumupha.’+ (Anthu onse azidzayankha kuti, ‘Zikhale momwemo!’)

25 ‘Wotembereredwa ndi munthu wolandira chiphuphu kuti aphe munthu wosalakwa.’+ (Anthu onse azidzayankha kuti, ‘Zikhale momwemo!’)

26 ‘Wotembereredwa ndi munthu amene sadzatsatira mawu a mʼChilamulo ichi ndipo sadzawagwiritsa ntchito.’+ (Anthu onse azidzayankha kuti, ‘Zikhale momwemo!’”)

28 “Mukamveradi mawu a Yehova Mulungu wanu poonetsetsa kuti mukutsatira malamulo ake onse amene ndikukupatsani lero, Yehova Mulungu wanu adzakukwezani ndithu pamwamba pa mitundu yonse ya padziko lapansi.+ 2 Mudzalandira madalitso onsewa ndipo zinthu zabwino zonsezi zidzakhala zanu,+ mukapitiriza kumvera mawu a Yehova Mulungu wanu:

3 Mudzakhala odalitsika mumzinda, komanso mudzakhala odalitsika mʼmunda.+

4 Ana anu+ adzakhala odalitsika* komanso chipatso cha mʼdziko lanu, ana a ziweto zanu, ana a ngʼombe zanu ndi ana a nkhosa zanu adzakhala odalitsika.+

5 Dengu+ lanu komanso chiwiya chanu chokandiramo ufa, zidzakhala zodalitsika.+

6 Mudzakhala odalitsika pa zochita zanu zonse.

7 Yehova adzachititsa adani anu amene adzakuukireni kugonja pamaso panu.+ Pobwera kudzakuukirani adzadutsa njira imodzi, koma pothawa pamaso panu, adzadutsa njira zosiyanasiyana 7.+ 8 Yehova adzadalitsa nyumba zanu zosungiramo zinthu+ komanso chilichonse chimene mukuchita ndipo adzakudalitsani mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani. 9 Yehova adzakupangani kukhala anthu ake oyera,+ mogwirizana ndi zimene analumbira kwa inu,+ chifukwa mukupitiriza kusunga malamulo a Yehova Mulungu wanu ndipo mukuyenda mʼnjira zake. 10 Anthu onse padziko lapansi adzaona kuti mukutchedwa ndi dzina la Yehova,+ ndipo adzachita nanu mantha.+

11 Yehova adzakupatsani ana ambiri komanso ziweto zochuluka ndipo nthaka+ yamʼdziko limene Yehova analumbira kwa makolo anu kuti adzakupatsani, idzabereka zipatso zambiri.+ 12 Yehova adzakutsegulirani kumwamba, nyumba yake yabwino yosungiramo zinthu, kuti akupatseni mvula pa nyengo yake+ mʼdziko lanu ndi kudalitsa chilichonse chimene mukuchita. Mudzakongoza mitundu yambiri koma inuyo simudzafunika kukongola kanthu kwa iwo.+ 13 Yehova adzakuchititsani kuti mukhale mutu osati mchira ndipo mudzakhala pamwamba+ osati mʼmunsi, mukapitiriza kumvera malamulo a Yehova Mulungu wanu amene ndikukupatsani lero kuti muziwasunga ndi kuwatsatira. 14 Musapatuke nʼkusiya kutsatira mawu onse amene ndikukulamulani lero, kupita kudzanja lamanja kapena lamanzere+ kuti mutsatire milungu ina nʼkuitumikira.+

15 Koma mukapanda kumvera mawu a Yehova Mulungu wanu poonetsetsa kuti mukutsatira malamulo ake onse ndi malangizo ake amene ndikukupatsani lero, mudzatembereredwa ndipo zinthu zoipa zotsatirazi zidzakuchitikirani:+

16 Mudzakhala otembereredwa mumzinda komanso mudzakhala otembereredwa mʼmunda.+

17 Dengu+ lanu komanso chiwiya chanu chokandiramo ufa zidzakhala zotembereredwa.+

18 Ana anu adzakhala otembereredwa*+ komanso chipatso cha nthaka yanu, ana a ngʼombe zanu ndi ana a nkhosa zanu adzakhala otembereredwa.+

19 Mudzakhala otembereredwa pa zochita zanu zonse.

20 Yehova adzakutumizirani matemberero, chisokonezo ndi chilango pa chilichonse chimene mukuchita mpaka mutawonongedwa nʼkutha mofulumira, chifukwa cha zinthu zoipa zimene mukuchita komanso chifukwa choti mwandisiya.+ 21 Yehova adzachititsa kuti matenda akukakamireni mpaka atakufafanizani mʼdziko limene mukupita kukalitenga kuti likhale lanu.+ 22 Yehova adzakulangani ndi chifuwa chachikulu, kutentha kwa thupi koopsa,+ kutupa, nyengo yotentha,* lupanga,+ mphepo yotentha yowononga mbewu ndi matenda a mbewu.+ Zimenezi zidzakuvutitsani mpaka mutatheratu. 23 Thambo limene lili pamwamba pa mutu wanu lidzakhala ngati kopa,* ndipo nthaka yanu idzakhala ngati chitsulo.+ 24 Yehova adzakugwetserani mchenga ndi fumbi ngati mvula mʼdziko lanu. Adzakugwetserani zimenezi kuchokera kumwamba mpaka mutawonongedwa. 25 Yehova adzachititsa kuti adani anu akugonjetseni.+ Popita kukawaukira mudzadutsa njira imodzi, koma pothawa mudzadutsa njira zosiyanasiyana 7. Mafumu onse a dziko lapansi adzachita mantha akadzaona zinthu zoipa zimene zakuchitikirani.+ 26 Mitembo yanu idzakhala chakudya cha mbalame zonse zouluka mumlengalenga ndi zilombo zoyenda panthaka, ndipo sipadzapezeka woziopseza.+

27 Yehova adzakulangani ndi zithupsa za ku Iguputo, matenda a mudzi,* ziwengo ndi zotupa, ndipo simudzachira matenda amenewa. 28 Yehova adzakulangani ndi misala, khungu+ ndipo adzakuchititsani kuti musokonezeke. 29 Mudzapapasapapasa masana ngati mmene munthu wavuto losaona amapapasira mumdima,+ ndipo chilichonse chimene mudzachite sichidzakuyenderani bwino. Nthawi zonse anthu azidzakuberani mwachinyengo komanso kukulandani zinthu zanu popanda wokupulumutsani.+ 30 Mudzalonjeza kukwatira mkazi koma mwamuna wina adzamugwiririra. Mudzamanga nyumba koma simudzakhalamo.+ Mudzadzala mitengo ya mpesa koma simudzadya zipatso zake.+ 31 Ngʼombe yanu idzaphedwa inu mukuona, koma simudzadya nyama yake. Bulu wanu adzabedwa inu mukuona ndipo simudzamuonanso. Nkhosa yanu idzaperekedwa kwa adani anu ndipo sipadzakhala wokupulumutsani. 32 Ana anu aamuna ndi ana anu aakazi adzaperekedwa kwa anthu ena+ inu mukuona ndipo nthawi zonse mudzalakalaka mutawaona, koma manja anu adzakhala opanda mphamvu. 33 Anthu amene simukuwadziwa adzadya zipatso zamʼdziko lanu ndi mbewu zanu zonse+ ndipo nthawi zonse muzidzaberedwa mwachinyengo komanso kuponderezedwa. 34 Mudzasokonezeka mutu chifukwa cha zimene maso anu adzaone.

35 Yehova adzakulangani ndi zithupsa zopweteka komanso zosachiritsika mʼmawondo ndi miyendo yanu. Matendawa adzayambira kumapazi mpaka paliwombo. 36 Yehova adzakuthamangitsani limodzi ndi mfumu yanu imene mudzaike kuti izikulamulirani, kukupititsani ku mtundu umene inuyo kapena makolo anu sanaudziwe.+ Kumeneko mudzatumikira milungu ina, milungu yamtengo ndi yamwala.+ 37 Anthu adzachita mantha akadzaona zimene zakuchitikirani ndipo mudzatonzedwa ndi kunyozedwa pakati pa mitundu yonse ya anthu kumene Yehova akukuthamangitsirani.+

38 Mudzadzala mbewu zambiri mʼmunda, koma mudzakolola zochepa+ chifukwa dzombe lidzadya mbewuzo. 39 Mudzalima nʼkudzala mitengo ya mpesa, koma simudzakolola mphesa zake nʼkumwa vinyo,+ chifukwa mbozi zidzadya mpesawo. 40 Mudzakhala ndi mitengo ya maolivi mʼdera lanu lonse, koma simudzadzola mafuta chifukwa maolivi anu adzayoyoka. 41 Mudzabereka ana aamuna ndi aakazi, koma sadzakhala anu chifukwa adzatengedwa kupita ku ukapolo.+ 42 Tizilombo timene timakhala tambirimbiri tidzawononga mitengo yanu yonse ndi zipatso za mʼdziko lanu. 43 Mlendo amene akukhala pakati panu adzapitiriza kukhala wamphamvu, koma inuyo mphamvu zanu zidzapitiriza kucheperachepera. 44 Iye adzakukongozani zinthu koma inuyo simudzatha kumukongoza.+ Iye adzakhala mutu koma inuyo mudzakhala mchira.+

45 Matemberero onsewa+ adzakugwerani ndipo zinthu zoipa zonsezi zidzakuchitikirani mpaka mutawonongedwa,+ chifukwa simunamvere mawu a Yehova Mulungu wanu posunga malamulo ndi malangizo amene anakupatsani.+ 46 Matembererowa adzapitiriza kugwera inu ndi ana anu ngati chizindikiro komanso chenjezo kwa inu mpaka kalekale,+ 47 chifukwa chakuti simunatumikire Yehova Mulungu wanu mokondwera komanso ndi mtima wosangalala, pamene munali ndi chilichonse komanso zinthu zochuluka.+ 48 Yehova adzakutumizirani adani anu kuti akuukireni ndipo mudzawatumikira+ muli ndi njala,+ ludzu, usiwa ndiponso mukusowa chilichonse. Iye adzakuvekani goli lachitsulo mʼkhosi lanu mpaka atakuwonongani.

49 Yehova adzatumiza mtundu wakutali+ kuchokera kumalekezero adziko lapansi kuti udzakuukireni. Mtunduwo udzakuukirani mofulumira kwambiri ngati mmene chiwombankhanga chimagwirira nyama.+ Mtundu umenewo chilankhulo chake simudzachimva,+ 50 mtundu wooneka moopsa umene sudzamvera chisoni munthu wachikulire kapena kuchitira chifundo mnyamata.+ 51 Iwo adzadya ana a ziweto zanu ndi zipatso za nthaka yanu mpaka mutawonongedwa. Sadzakusiyirani mbewu iliyonse, vinyo watsopano kapena mafuta, mwana wa ngʼombe kapena mwana wa nkhosa mpaka atakuwonongani.+ 52 Adzakuzungulirani nʼkukutsekerani mʼmizinda yanu* mʼdziko lanu lonse, mpaka mipanda yanu yaitali ndi yolimba kwambiri imene mukuidalira itagwa. Adzakuzungulirani ndithu mʼmizinda yanu yonse mʼdziko lanu limene Yehova Mulungu wanu wakupatsani.+ 53 Zikadzatero mudzadya ana anu omwe,* mnofu wa ana anu aamuna ndi ana anu aakazi+ amene Yehova Mulungu wanu wakupatsani, chifukwa cha mavuto oopsa amene mudzakumane nawo adani anu akadzakuzungulirani.

54 Ngakhale mwamuna amene ndi wachifundo komanso wofatsa pakati panu, sadzachitira chisoni mchimwene wake, mkazi wake wokondedwa ndi ana ake aamuna amene atsala, 55 ndipo sadzagawana nawo mnofu uliwonse wa ana ake aamuna amene adzawadye, popeza adzakhala alibiretu china chilichonse chifukwa cha mavuto oopsa amene mudzakumane nawo adani anu akadzazungulira mizinda yanu.+ 56 Ndipo mkazi amene anakulira moyo wofewa komanso wachisasati pakati panu, amene sanayambe waganizapo zopondetsa phazi lake pansi chifukwa chokulira moyo wofewa, sadzamvera chisoni mwamuna wake wokondedwa,+ mwana wake wamwamuna komanso mwana wake wamkazi. 57 Iye sadzafuna kugawana nawo zotuluka mʼmimba mwake pambuyo pobereka komanso mnofu wa ana ake aamuna amene wabereka, popeza adzawadya mobisa chifukwa cha mavuto oopsa amene mudzakumane nawo adani anu akadzazungulira mizinda yanu.

58 Ngati simudzatsatira mosamala mawu onse a Chilamulo ichi amene alembedwa mʼbuku ili,+ ndipo ngati simudzaopa dzina laulemerero ndi lochititsa manthali,+ dzina la Yehova+ Mulungu wanu, 59 Yehova adzabweretsa miliri yoopsa pa inu ndi ana anu. Miliri imeneyo idzakhala yaikulu kwambiri ndi yokhalitsa,+ ndipo mudzagwidwa ndi matenda oopsa komanso okhalitsa. 60 Adzakubweretserani matenda onse a ku Iguputo amene munkachita nawo mantha, ndipo simudzachira. 61 Kuwonjezera pamenepo, Yehova adzakubweretserani matenda aliwonse ndi mliri uliwonse umene sunalembedwe mʼbuku la Chilamulo ili, mpaka mutawonongedwa. 62 Ngakhale kuti mwachuluka ngati nyenyezi zakumwamba,+ mudzatsala ochepa+ chifukwa chakuti simunamvere mawu a Yehova Mulungu wanu.

63 Mofanana ndi mmene Yehova anasangalalira kuchititsa kuti zinthu zikuyendereni bwino komanso kuchititsa kuti muchuluke, Yehova adzasangalalanso kuti akuwonongeni nʼkukufafanizani, ndipo mudzatheratu mʼdziko limene mukupita kukalitenga kuti likhale lanu.

64 Yehova adzakubalalitsirani pakati pa mitundu yonse, kuchokera kumalekezero a dziko mpaka kumalekezero ena a dziko.+ Kumeneko mudzatumikira milungu yamtengo komanso milungu yamwala, imene inuyo kapena makolo anu sanaidziwe.+ 65 Mudzasowa mtendere pakati pa mitundu imeneyo,+ ndipo simudzapeza malo oti phazi lanu liponde kuti lipume. Mʼmalomwake, Yehova adzakupatsani mtima wankhawa,+ adzachititsa kuti maso anu aziona movutikira ndipo adzakuchititsani kuti mutaye mtima.+ 66 Moyo wanu udzakhala pangozi yaikulu koopsa, ndipo mudzakhala mwamantha usiku ndi masana, moti simudzakhala wotsimikiza ngati mudzakhalebe ndi moyo. 67 Mʼmawa mudzanena kuti, ‘Zikanakhala bwino akanakhala madzulo!’ ndipo madzulo mudzanena kuti, ‘Zikanakhala bwino ukanakhala mʼmawa!’ chifukwa cha mantha amene adzagwire mtima wanu, ndiponso chifukwa cha zimene maso anu adzaone. 68 Yehova adzakubwezerani ku Iguputo pasitima kudzera njira imene ndinakuuzani kuti, ‘Simudzaionanso.’ Kumeneko mudzalakalaka kudzigulitsa kwa adani anu kuti mukhale akapolo aamuna ndi aakazi, koma sipadzakhala wokugulani.”

29 Awa ndi mawu a pangano limene Yehova analamula Mose kuti achite ndi Aisiraeli mʼdziko la Mowabu, kuwonjezera pa pangano limene anachita nawo ku Horebe.+

2 Choncho Mose anaitana Aisiraeli onse nʼkuwauza kuti: “Inu munaona ndi maso anu mʼdziko la Iguputo zonse zimene Yehova anachitira Farao, atumiki ake onse ndi dziko lake lonse,+ 3 ziweruzo zamphamvu zimene* maso anu anaona, kapena kuti zizindikiro zazikulu komanso zodabwitsa.+ 4 Koma Yehova sanakupatseni mtima woti muthe kumvetsa zinthu, maso oti muthe kuona ndi makutu oti muthe kumva, mpaka lero.+ 5 ‘Pamene ndinkakutsogolerani kwa zaka 40 mʼchipululu,+ zovala zanu sizinathe ndiponso nsapato zanu sizinathe kumapazi anu.+ 6 Simunadye mkate, simunamwe vinyo kapena zakumwa zina zoledzeretsa, kuti mudziwe kuti ine ndine Yehova Mulungu wanu.’ 7 Ndiyeno munafika pamalo ano, ndipo Sihoni mfumu ya Hesiboni+ ndi Ogi mfumu ya Basana+ anabwera kudzamenyana nafe, koma tinawagonjetsa.+ 8 Kenako tinatenga dziko lawo nʼkulipereka ngati cholowa kwa fuko la Rubeni, fuko la Gadi ndi hafu ya fuko la Manase.+ 9 Choncho muzisunga mawu a pangano ili komanso kuwamvera kuti zonse zimene muzichita zizikuyenderani bwino.+

10 Nonsenu mwaima pano lero pamaso pa Yehova Mulungu wanu, inu atsogoleri a mafuko, akulu anu, atsogoleri anu, mwamuna aliyense wa mu Isiraeli, 11 ana anu, akazi anu,+ mlendo+ amene akukhala mumsasa wanu, kuyambira amene amakutolerani nkhuni mpaka amene amakutungirani madzi. 12 Inu muli pano kuti mulumbire nʼkuchita pangano ndi Yehova Mulungu wanu, pangano limene Yehova Mulungu wanu akuchita nanu lero.+ 13 Cholinga chake nʼchakuti lero akupangeni kuti mukhale anthu ake+ komanso kuti iye akhale Mulungu wanu,+ mogwirizana ndi zimene anakulonjezani ndiponso mogwirizana ndi zimene analumbira kwa makolo anu, Abulahamu,+ Isaki+ ndi Yakobo.+

14 Tsopano sindikuchita pangano ili komanso kulumbiritsa inu nokha ayi, 15 koma ndikuchitanso zimenezi ndi anthu amene aimirira ndi ife pano lero pamaso pa Yehova Mulungu wathu, komanso ndi anthu amene sitili nawo pano lero. 16 (Pakuti inu mukudziwa bwino mmene tinkakhalira mʼdziko la Iguputo komanso mmene tinadutsira pakati pa anthu a mitundu ina pa ulendo wathuwu.+ 17 Inu munkaona zinthu zawo zonyansa ndi mafano awo onyansa*+ amtengo ndi amwala, asiliva ndi agolide amene anali pakati pawo.) 18 Samalani kuti pakati panu lero pasapezeke mwamuna, mkazi, banja kapena fuko limene mtima wake wapatuka kusiya Yehova Mulungu wathu nʼkupita kukatumikira milungu ya mitundu inayo,+ kuti pakati panu pasapezeke muzu wotulutsa chipatso chapoizoni komanso chitsamba chowawa.+

19 Koma ngati wina wamva mawu a lumbiro ili nʼkulankhula modzitama mumtima mwake kuti, ‘Ndikhala ndi mtendere ngakhale kuti ndikuyendabe motsatira zofuna za mtima wanga,’ zimene zidzachititse kuti aliyense woyandikana naye* awonongedwe, 20 Yehova sadzafuna kukhululukira munthu woteroyo.+ Mʼmalomwake, mkwiyo waukulu wa Yehova udzamuyakira, ndipo matemberero onse amene alembedwa mʼbuku ili adzamugwera,+ ndipo Yehova adzachotseratu dzina la munthuyo pansi pa thambo. 21 Kenako Yehova adzamupatula pa mafuko onse a Isiraeli kuti amubweretsere tsoka, mogwirizana ndi matemberero onse amene adzagwere anthu ophwanya pangano limene lalembedwa mʼbuku la Chilamulo ili.

22 Mʼbadwo wa mʼtsogolo wa ana anu ndiponso mlendo wochokera kudziko lakutali, akadzaona miliri ndi matenda amene Yehova wabweretsa mʼdzikoli—* 23 akadzaona kuti dziko lonse lawonongedwa ndi sulufule, mchere ndi kutentha, moti mʼdzikomo simungadzalidwe mbewu, simungaphuke kalikonse ndipo simungamere chomera chilichonse, ndipo likuoneka ngati Sodomu ndi Gomora,+ Adima ndi Zeboyimu,+ mizinda imene Yehova anaiwononga ndi ukali komanso mkwiyo wake—* 24 ana anu ndi alendo komanso mitundu yonse adzanena kuti, ‘Nʼchifukwa chiyani Yehova wachitira dzikoli zimenezi?+ Nʼchiyani chachititsa kuti mkwiyo wake uyake kwambiri chonchi?’ 25 Ndiyeno iwo adzanena kuti, ‘Nʼchifukwa chakuti anaphwanya pangano la Yehova,+ Mulungu wa makolo awo, limene anapangana nawo pamene ankawatulutsa mʼdziko la Iguputo.+ 26 Koma iwo anapita kukatumikira milungu ina ndi kuigwadira, milungu imene sankaidziwa komanso imene sanawalole kuti aziilambira.+ 27 Zitatero mkwiyo wa Yehova unayakira dziko limeneli ndipo analibweretsera matemberero onse amene analembedwa mʼbuku ili.+ 28 Choncho Yehova anawazula mʼdziko lawo atapsa mtima,+ ali ndi ukali ndiponso mkwiyo waukulu nʼkuwapititsa kudziko lina, kumene ali lero.’+

29 Yehova Mulungu wathu+ amadziwa zinthu zonse zobisika, koma amaulula zinthu kwa ifeyo komanso kwa zidzukulu zathu ku mibadwomibadwo, kuti titsatire mawu onse a Chilamulo ichi.”+

30 “Mawu onsewa akadzakwaniritsidwa pa inu, madalitso ndi matemberero amene ndaika pamaso panu,+ ndipo mukadzawakumbukira*+ muli ku mitundu yonse kumene Yehova Mulungu wanu adzakubalalitsireni,+ 2 inu nʼkubwerera kwa Yehova Mulungu wanu+ komanso kumvera mawu ake ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse, mogwirizana ndi zonse zimene ndikukulamulani lero, inuyo ndi ana anu,+ 3 Yehova Mulungu wanu adzabweza kwawo anthu a mtundu wanu amene anagwidwa nʼkupita kudziko lina,+ ndipo adzakuchitirani chifundo+ nʼkukusonkhanitsaninso pamodzi kuchokera pakati pa anthu onse kumene Yehova Mulungu wanu anakubalalitsirani.+ 4 Ngakhale anthu a mtundu wanu amene anabalalitsidwawo atadzakhala kumalekezero kwa thambo, Yehova Mulungu wanu adzakusonkhanitsani nʼkukubweretsani kuchokera kumeneko.+ 5 Yehova Mulungu wanu adzakubweretsani mʼdziko limene makolo anu analitenga kuti likhale lawo, ndipo lidzakhala lanu. Iye adzachititsa kuti zinthu zikuyendereni bwino ndipo adzakuchulukitsani kwambiri kuposa makolo anu.+ 6 Yehova Mulungu wanu adzayeretsa* mitima yanu ndi mitima ya ana anu,+ kuti muzikonda Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse komanso moyo wanu wonse ndipo mudzakhala ndi moyo.+ 7 Ndiyeno Yehova Mulungu wanu adzabweretsa matemberero onsewa pa adani anu, amene ankadana nanu komanso kukuzunzani.+

8 Kenako inu mudzabwerera nʼkumvera mawu a Yehova komanso kutsatira malamulo ake onse amene ndikukupatsani lero. 9 Yehova Mulungu wanu adzachititsa kuti zinthu zikuyendereni bwino kwambiri pa ntchito iliyonse ya manja anu.+ Adzachulukitsa ana anu, ziweto zanu ndi zokolola zanu, chifukwa Yehova adzasangalalanso kuchititsa kuti zinthu zikuyendereni bwino, ngati mmene anachitira ndi makolo anu.+ 10 Chifukwa pa nthawiyo mudzamvera mawu a Yehova Mulungu wanu ndi kusunga malamulo komanso malangizo ake amene analembedwa mʼbuku ili la Chilamulo, ndipo mudzabwerera kwa Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse komanso moyo wanu wonse.+

11 Lamulo limene ndikukupatsani leroli si lovuta kwa inu kulitsatira, ndipo silili poti simungathe kulipeza.*+ 12 Silili kumwamba kuti munene kuti, ‘Ndani adzapite kumwamba kuti akatitengere lamulolo kuti ife tidzalimve nʼkulitsatira?’+ 13 Ndiponso silili tsidya lina la nyanja kuti munene kuti, ‘Ndani adzawoloke kupita tsidya lina la nyanja kuti akatitengere lamulolo kuti ife tidzalimve nʼkulitsatira?’ 14 Chifukwa mawu a chilamulowo ali pafupi kwambiri ndi inu, ali mʼkamwa mwanu ndi mumtima mwanu+ kuti muwatsatire.+

15 Taonani, ine ndikuika pamaso panu lero moyo ndi zinthu zabwino, imfa ndi zinthu zoipa.+ 16 Mukadzamvera malamulo a Yehova Mulungu wanu amene ndikukupatsani lero, pokonda Yehova Mulungu wanu,+ kuyenda mʼnjira zake ndi kusunga malamulo ake, malangizo ake ndi zigamulo zake, mudzakhala ndi moyo,+ mudzachulukana ndipo Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani mʼdziko limene mukupita kukalitenga kuti likhale lanu.+

17 Koma mtima wanu ukatembenukira kwina+ ndipo simukumvera, moti mwakopeka nʼkugwadira milungu ina ndi kuitumikira,+ 18 ndikukuuzani lero kuti mudzatheratu.+ Simudzakhala nthawi yaitali mʼdziko limene mukupita kukalitenga kuti likhale lanu mutawoloka Yorodano. 19 Lero ndaika moyo ndi imfa, dalitso ndi temberero pamaso panu.+ Kumwamba ndi dziko lapansi ndi mboni pa zochita zanu. Choncho inuyo ndi mbadwa zanu+ musankhe moyo kuti mukhalebe ndi moyo.+ 20 Musankhe moyo pokonda Yehova Mulungu wanu,+ kumvera mawu ake ndi kukhala okhulupirika kwa iye,+ chifukwa iye ndi amene amapereka moyo ndipo angakuthandizeni kuti mukhale ndi moyo kwa nthawi yaitali mʼdziko limene Yehova analumbira kuti adzalipereka kwa makolo anu, Abulahamu, Isaki ndi Yakobo.”+

31 Kenako Mose anapita kukauza Aisiraeli onse mawu awa, 2 kuti: “Tsopano ndili ndi zaka 120.+ Sindingathenso kukutsogolerani* chifukwa Yehova wandiuza kuti, ‘Suwoloka Yorodano uyu.’+ 3 Yehova Mulungu wanu akuwoloka patsogolo panu kuti akutsogolereni. Iye adzawononga mitundu imeneyi pamaso panu ndipo inu mudzaithamangitsa.+ Yoswa ndi amene akutsogolereni nʼkukuwolotsani,+ mogwirizana ndi zimene Yehova wanena. 4 Yehova adzachitira mitundu imeneyi zimene anachitira Sihoni+ ndi Ogi,+ mafumu a Aamori, ndiponso zimene anachitira dziko lawo pamene anawawononga.+ 5 Yehova adzakugonjetserani mitundu imeneyi, ndipo mudzaichitire mogwirizana ndi malamulo onse amene ndakupatsani.+ 6 Limbani mtima ndipo muchite zinthu mwamphamvu.+ Musawaope kapena kuchita nawo mantha,+ chifukwa Yehova Mulungu wanu ndi amene akuyenda patsogolo panu. Iye sadzakutayani kapena kukusiyani ngakhale pangʼono.”+

7 Kenako Mose anaitana Yoswa nʼkumuuza pamaso pa Aisiraeli onse kuti: “Limba mtima ndipo uchite zinthu mwamphamvu,+ chifukwa iwe ndi amene udzalowetse anthu awa mʼdziko limene Yehova analumbira kwa makolo awo kuti adzawapatsa. Ndipo iwe ndi amene udzawagawire dzikolo kuti likhale cholowa chawo.+ 8 Yehova ndi amene akuyenda patsogolo panu ndipo apitiriza kuyenda nanu.+ Sadzakutayani kapena kukusiyani ngakhale pangʼono. Choncho musaope kapena kuchita mantha.”+

9 Kenako Mose analemba Chilamulo+ chimenechi nʼkuchipereka kwa ansembe, omwe ndi Alevi, amene amanyamula likasa la pangano la Yehova, komanso kwa akulu onse a Isiraeli. 10 Ndiyeno Mose anawalamula kuti: “Kumapeto kwa zaka 7 zilizonse, pa nthawi imene inaikidwiratu mʼchaka choti anthu angongole amasuke,+ Pachikondwerero cha Misasa,+ 11 Aisiraeli onse akabwera pamaso pa Yehova+ Mulungu wanu pamalo amene iye adzasankhe, muzidzawerenga Chilamulo ichi pamaso pa Aisiraeli onse kuti achimve.+ 12 Sonkhanitsani anthu,+ amuna, akazi, ana ndi alendo amene akukhala mʼmizinda yanu,* kuti amvetsere komanso kuti aphunzire zokhudza Yehova Mulungu wanu, kuti azimuopa ndiponso kuti azitsatira mosamala mawu onse a mʼChilamulo ichi. 13 Akatero ana awo amene sakudziwa Chilamulo ichi adzamvetsera+ ndipo adzaphunzira kuopa Yehova Mulungu wanu, masiku onse amene mudzakhale mʼdziko limene mukuwoloka Yorodano kukalitenga kuti likhale lanu.”+

14 Kenako Yehova anauza Mose kuti: “Taona, nthawi yoti ufe yayandikira.+ Itana Yoswa, ndipo mukaime pachihema chokumanako kuti ndikamuike kukhala mtsogoleri.”+ Choncho Mose ndi Yoswa anapita nʼkukaima pachihema chokumanako. 15 Ndiyeno Yehova anaonekera kuchihemako mʼchipilala cha mtambo chimene chinaima pafupi ndi khomo la chihema.+

16 Tsopano Yehova anauza Mose kuti: “Iweyo watsala pangʼono kufa,* ndipo anthu awa adzakhala osakhulupirika kwa ine ndipo adzayamba kulambira milungu yachilendo imene ili mʼdziko limene akupita.+ Iwo adzandisiya+ nʼkuphwanya pangano limene ndinapangana nawo.+ 17 Pa nthawi imeneyo mkwiyo wanga udzawayakira+ ndipo ndidzawasiya+ nʼkuwabisira nkhope yanga+ mpaka atawonongedwa.+ Ndiyeno akadzakumana ndi masoka komanso mavuto ambiri adzanena kuti, ‘Masoka amenewatu akutigwera chifukwa chakuti Mulungu wathu sali pakati pathu.’+ 18 Koma ine ndidzapitiriza kuwabisira nkhope yanga pa tsiku limenelo chifukwa cha zoipa zonse zimene achita, potembenukira kwa milungu ina.+

19 Tsopano mulembe nyimbo iyi+ nʼkuphunzitsa Aisiraeli.+ Muwaphunzitse* nyimbo imeneyi kuti ikhale mboni yanga pamaso pa Aisiraeliwo.+ 20 Ndikadzawalowetsa mʼdziko limene ndinalumbira kwa makolo awo,+ dziko loyenda mkaka ndi uchi,+ ndipo akadzadya nʼkukhuta, zinthu nʼkuyamba kuwayendera bwino,*+ adzatembenukira kwa milungu ina nʼkuyamba kuitumikira. Iwo adzandichitira mwano komanso kuphwanya pangano langa.+ 21 Ndiyeno akadzakumana ndi masoka komanso mavuto ambiri,+ nyimboyi idzawakumbutsa zimene ndinawachenjeza, (chifukwa mbadwa zawo sizikuyenera kuiwala nyimboyi), chifukwa ndikudziwa kale mtima umene ayamba kukhala nawo+ ndisanawalowetse nʼkomwe mʼdziko limene ndinawalumbirira.”

22 Choncho Mose analemba nyimboyi pa tsiku limenelo nʼkuphunzitsa Aisiraeli.

23 Ndiyeno Mulungu anaika Yoswa+ mwana wa Nuni kuti akhale mtsogoleri, ndipo anamuuza kuti: “Limba mtima ndipo uchite zinthu mwamphamvu,+ chifukwa iwe ndi amene udzalowetse Aisiraeli mʼdziko limene ndawalumbirira,+ ndipo ine ndidzapitiriza kukhala ndi iwe.”

24 Mose atangomaliza kulemba mawu onse a Chilamulo ichi mʼbuku,+ 25 Mose analamula Alevi amene amanyamula likasa la pangano la Yehova kuti: 26 “Tengani buku ili la Chilamulo+ ndipo muliike pambali pa likasa+ la pangano la Yehova Mulungu wanu, ndipo lidzakhala mboni ya Mulungu yokutsutsani. 27 Ineyo ndikudziwa bwino khalidwe lanu lopanduka+ ndi kuuma mtima* kwanu.+ Ngati mwakhala mukupandukira Yehova pamene ndili moyo, ndiye kuli bwanji pambuyo pa imfa yanga! 28 Sonkhanitsani akulu onse a mafuko anu ndi atsogoleri anu, kuti amve mawu awa amene ndikufuna kulankhula nawo, ndipo nditenge kumwamba ndi dziko lapansi kuti zikhale mboni zanga pamaso pawo.+ 29 Chifukwa ndikudziwa bwino kuti pambuyo pa imfa yanga, mosakayikira mudzachita zinthu zoipa+ nʼkupatuka kusiya njira imene ndakulamulani. Ndiyeno pamapeto pake tsoka lidzakugwerani,+ chifukwa mudzachita zoipa pamaso pa Yehova ndipo mudzamukhumudwitsa ndi ntchito za manja anu.”

30 Choncho mpingo wonse wa Isiraeli ukumva, Mose anayamba kulankhula mawu a nyimbo iyi, kuchokera poyambirira mpaka kumapeto kuti:+

32 “Tamverani kumwamba inu, ndipo ine ndilankhula,

Dziko lapansi limve mawu a pakamwa panga.

 2 Malangizo anga adzagwa ngati mvula,

Mawu anga adzatsika ngati mame,

Ngati mvula yowaza pa udzu,

Ngatinso mvula yamphamvu pazomera.

 3 Chifukwa ndidzalengeza dzina la Yehova.+

Anthu inu, lengezani za ukulu wa Mulungu wathu!+

 4 Iye ndi Thanthwe, ndipo ntchito yake ndi yangwiro,+

Njira zake zonse ndi zolungama.+

Mulungu wokhulupirika,+ amene sachita zinthu zopanda chilungamo.+

Iye ndi wolungama ndi wowongoka.+

 5 Iwo ndi amene achita zinthu zoipa.+

Iwo si ana ake, ali ndi vuto ndi iwowo.+

Iwo ndi mʼbadwo wopotoka maganizo komanso wachinyengo!+

 6 Kodi Yehova mukuyenera kumuchitira zimenezi,+

Anthu opusa ndi opanda nzeru inu?+

Kodi iye si Atate wanu amene anakulengani,+

Amene anakupangani ndi kukukhazikitsani monga mtundu?

 7 Kumbukirani masiku akale,

Ganizirani zaka za mibadwo ya mʼmbuyo.

Funsani bambo anu ndipo akuuzani,+

Amuna achikulire pakati panu, ndipo akufotokozerani.

 8 Pamene Wamʼmwambamwamba anapereka cholowa ku mitundu ya anthu,+

Pamene analekanitsa ana a Adamu,*+

Anaika malire a anthu ena onse+

Poganizira chiwerengero cha ana a Isiraeli.+

 9 Pakuti anthu a Yehova ndi gawo lake.+

Yakobo ndiye cholowa chake.+

10 Anamupeza mʼdziko lachipululu,+

Mʼchipululu chopanda kanthu, molira zilombo.+

Anamuzungulira kuti amuteteze, anamusamalira,+

Ndipo anamuteteza ngati mwana wa diso lake.+

11 Monga mmene chiwombankhanga chimagwedezera chisa chake,

Mmene chimaulukira pamwamba pa ana ake,

Mmene chimatambasulira mapiko ake, kuti chitenge anawo,

Nʼkuwanyamula pamapiko ake,+

12 Ndi Yehova yekha amene anapitiriza kumutsogolera,*+

Panalibe mulungu wachilendo amene anali naye.+

13 Anamuyendetsa pamapiri a dziko lapansi,+

Moti anadya zokolola za mʼmunda.+

Anamudyetsa uchi wochokera mʼthanthwe,

Ndi mafuta ochokera mʼmwala wa nsangalabwi.

14 Anamudyetsanso mafuta a mkaka wa ngʼombe ndi mkaka wa nkhosa,

Pamodzi ndi nkhosa zabwino kwambiri,*

Komanso nkhosa zamphongo za ku Basana ndi mbuzi zamphongo,

Pamodzi ndi tirigu wabwino koposa.*+

Ndipo munamwa vinyo wochokera mʼmagazi a mphesa.*

15 Yesuruni* atanenepa, anapandukira mbuye wake.

Iwe wanenepa, wakula thupi, wakhuta mopitirira muyezo.+

Choncho iye anasiya Mulungu amene anamupanga,+

Ndipo ananyoza Thanthwe la chipulumutso chake.

16 Anamukwiyitsa ndi milungu yachilendo.+

Ankamukhumudwitsa ndi zinthu zonyansa.+

17 Iwo ankapereka nsembe kwa ziwanda, osati kwa Mulungu.+

Anapereka nsembe kwa milungu imene sankaidziwa,

Kwa milungu yatsopano yongobwera kumene,

Komanso kwa milungu imene makolo anu sankaidziwa.

18 Munaiwala Thanthwe+ limene linakuberekani,

Ndipo simunakumbukire Mulungu amene anakuberekani.+

19 Yehova ataona zimenezi anawakana+

Chifukwa chakuti ana ake aamuna ndi aakazi anamukhumudwitsa.

20 Choncho iye anati, ‘Ndiwabisira nkhope yanga,+

Ndione kuti ziwathera bwanji.

Chifukwa iwo ndi mʼbadwo wokonda zoipa,+

Ana osakhulupirika.+

21 Iwo andikwiyitsa* ndi milungu yabodza.+

Andikhumudwitsa ndi mafano awo opanda pake.+

Choncho ine ndiwachititsa nsanje ndi anthu opanda pake,+

Ndiwakhumudwitsa ndi mtundu wopusa.+

22 Mkwiyo wanga wayatsa moto+

Umene udzayaka mpaka kukafika pansi penipeni pa Manda,*+

Ndipo udzapsereza dziko lapansi ndi zokolola zake,

Komanso udzayatsa maziko a mapiri.

23 Ndidzawonjezera masoka awo,

Mivi yanga yonse ndidzaigwiritsa ntchito pa iwo.

24 Adzalefuka ndi njala+

Ndipo adzavutika ndi kutentha thupi koopsa komanso adzawonongedwa nʼkutheratu.+

Ndidzawatumizira zilombo za mano ataliatali+

Komanso njoka zapoizoni za mʼfumbi.

25 Kunja, lupanga lidzawasandutsa anamfedwa.+

Mʼnyumba, anthu adzagwidwa ndi mantha+

Zimenezi zidzachitikira mnyamata, namwali,

Mwana wamngʼono ndi munthu wa imvi.+

26 Ndikanatha kunena kuti: “Ndidzawabalalitsa,

Ndidzachititsa kuti anthu asakumbukirenso za iwo,”

27 Koma ndinkaopa zimene mdani anganene,+

Chifukwa adaniwo angaganize molakwika.+

Iwo anganene kuti: “Tapambana chifukwa cha mphamvu zathu,+

Si Yehova amene wachita zonsezi.”

28 Chifukwa iwo ndi mtundu wopanda nzeru,*

Ndipo ndi osazindikira.+

29 Zikanakhala bwino ngati akanakhala anzeru,+ chifukwa akanaganizira mozama zimenezi.+

Akanaganizira kuti ziwathera bwanji.+

30 Kodi munthu mmodzi angathamangitse bwanji anthu 1,000,

Kapena anthu awiri angathamangitse bwanji anthu 10,000?+

Nʼzosatheka, pokhapokha Thanthwe lawo litawagulitsa,+

Komanso ngati Yehova atawapereka.

31 Chifukwa thanthwe lawo si lofanana ndi Thanthwe lathu,+

Ndipo adani athu akudziwa bwino zimenezi.+

32 Mtengo wawo wa mpesa ndi wochokera ku mtengo wa mpesa wa ku Sodomu,

Ndi kuminda ya mʼmapiri a ku Gomora.+

Zipatso zawo za mphesa ndi zapoizoni

Ndipo ndi zowawa.+

33 Vinyo wawo ndi poizoni wa njoka,

Ndi poizoni woopsa wa mamba.

34 Kodi ine sindinasunge zimenezi,

Nʼkuziikira chidindo mʼnyumba yanga yosungira zinthu?+

35 Kubwezera ndi kwanga, chilangonso ndi changa.+

Zimenezi zidzachitika pa nthawi yoikidwiratu phazi lawo likadzaterereka,+

Chifukwa tsiku la tsoka lawo layandikira,

Ndipo zowagwera zifika mofulumira.’

36 Pakuti Yehova adzaweruza anthu ake,+

Ndipo adzamvera chisoni atumiki ake+

Akadzaona kuti mphamvu zawo zatha,

Komanso kuti kwangotsala anthu ovutika ndi ofooka.

37 Ndiyeno iye adzanena kuti, ‘Ili kuti milungu yawo,+

Thanthwe limene anathawirako,

38 Milungu imene inkadya mafuta a nsembe zawo,*

Ndi kumwa vinyo wa nsembe zawo zachakumwa?+

Ibwere kudzakuthandizani.

Ikhale malo anu othawirako.

39 Onani tsopano kuti ndine Mulungu,+

Ndipo palibe Mulungu wina koma ine ndekha.+

Ndimapha komanso ndimapereka moyo.+

Ndimavulaza,+ ndipo ndidzachiritsa,+

Palibe aliyense amene angapulumutse munthu mʼdzanja langa.+

40 Ndakweza dzanja langa kumwamba

Ndipo ndikulumbira kuti: “Ine, Mulungu wamuyaya, ndikulumbira pa dzina langa,”+

41 Ndikanola lupanga langa lonyezimira,

Nʼkukonzekeretsa dzanja langa kuti lipereke chiweruzo,+

Ndidzabwezera adani anga,+

Ndipo ndidzapereka chilango kwa amene amadana nane.

42 Ndidzaledzeretsa mivi yanga ndi magazi,

Ndipo lupanga langa lidzadya nyama,

Ndi magazi a anthu ophedwa komanso ogwidwa,

Ndiponso mitu ya atsogoleri a adani.’

43 Inu anthu a mitundu ina, sangalalani limodzi ndi anthu ake,+

Chifukwa adzabwezera magazi a atumiki ake,+

Ndipo adzabwezera chilango kwa adani ake,+

Komanso adzaphimba machimo a dziko la anthu ake.”*

44 Ndiyeno Mose anabwera nʼkulankhula mawu onse a nyimbo iyi anthu onse akumva,+ iye pamodzi ndi Hoshiya*+ mwana wa Nuni. 45 Mose atamaliza kulankhula mawu onsewa kwa Aisiraeli onse, 46 anawauza kuti: “Ganizirani mofatsa mawu onse okuchenjezani amene ndikulankhula nanu lero,+ kuti muuze ana anu kuti azionetsetsa kuti akuchita zimene mawu onse a Chilamulo ichi akunena.+ 47 Chifukwa amenewa si mawu opanda pake kwa inu, koma angakuthandizeni kukhala ndi moyo.+ Mukamatsatira mawu amenewa mudzakhala ndi moyo wautali mʼdziko limene mukuwoloka Yorodano kuti mukalitenge kukhala lanu.”

48 Yehova analankhula ndi Mose pa tsiku lomweli kuti: 49 “Kwera mʼphiri ili la Abarimu,+ phiri la Nebo,+ limene lili mʼdziko la Mowabu, moyangʼanizana ndi Yeriko, ndipo uone dziko la Kanani limene ndikupereka kwa Aisiraeli kuti likhale lawo.+ 50 Kenako ukafera paphiri limene ukufuna kukwerali nʼkuikidwa mʼmanda ngati mmene anachitira ndi makolo ako,* mofanana ndi Aroni mʼbale wako amene anafera paphiri la Hora+ nʼkuikidwa mʼmanda ngati mmene anachitira ndi makolo ake. 51 Izi zili choncho chifukwa awirinu simunakhale okhulupirika kwa ine pakati pa Aisiraeli kumadzi a pa Meriba+ ku Kadesi, mʼchipululu cha Zini, chifukwa simunandilemekeze pamaso pa Aisiraeli.+ 52 Iwe udzaona dzikolo uli patali, koma sudzalowa mʼdziko limene ndikupereka kwa Aisiraeli.”+

33 Tsopano awa ndi madalitso amene Mose, munthu wa Mulungu woona, ananena asanafe kuti Aisiraeli adzalandira.+ 2 Iye anati:

“Yehova anabwera kuchokera ku Sinai,+

Anawala pa iwo kuchokera ku Seiri.

Anawala mwa ulemerero kuchokera kudera lamapiri la Parana,+

Ndipo anali ndi angelo ake ambirimbiri,*+

Kudzanja lake lamanja kunali asilikali ake.+

 3 Iye ankakonda anthu ake,+

Anthu oyera onsewa ali mʼmanja mwanu.+

Iwowa anakhala pamapazi anu.+

Anayamba kumvetsera mawu anu.+

 4 (Mose anatipatsa chilamulo,+

Chimene ndi chuma cha mpingo wa Yakobo.)+

 5 Mulungu anakhala mfumu mu Yesuruni,*+

Pamene atsogoleri a anthu anasonkhana pamodzi,+

Limodzi ndi mafuko onse a Isiraeli.+

 6 Rubeni akhale ndi moyo ndipo asafe,+

Ndipo anthu ake asakhale ochepa.”+

 7 Iye ananena kuti Yuda adzalandira madalitso otsatirawa:+

“Inu Yehova, imvani mawu a Yuda,+

Ndipo mumubwezere kwa anthu ake.

Iye wateteza* zinthu zake ndi manja ake,

Mumuthandize kulimbana ndi adani ake.”+

 8 Ponena za Levi anati:+

“Tumimu ndi Urimu wanu*+ ndi za munthu wokhulupirika kwa inu,+

Amene munamuyesa pa Masa.+

Munayamba kulimbana naye pafupi ndi madzi a ku Meriba.+

 9 Munthu amene anauza bambo ndi mayi ake kuti, ‘Sindinasonyeze kuti ndikuwalabadira.’

Ngakhale abale ake sanawasamale,+

Ndipo ana ake anakhala ngati sakuwadziwa.

Chifukwa anatsatira mawu anu,

Ndipo anasunga pangano lanu.+

10 Amenewa azilangiza Yakobo pa zigamulo zanu+

Ndi Isiraeli mʼChilamulo chanu.+

Azipereka nsembe zofukiza kuti zikhale kafungo kosangalatsa kwa inu,*+

Ndi nsembe yathunthu paguwa lanu lansembe.+

11 Inu Yehova dalitsani mphamvu zake,

Ndipo mukondwere ndi ntchito ya manja ake.

Muphwanye miyendo ya* amene akumuukira,

Kuti amene amadana naye asathenso kuimirira.”

12 Ponena za Benjamini anati:+

“Wokondedwa wa Yehova azikhala wotetezedwa ndi iye,

Pamene akumuteteza tsiku lonse,

Iye adzakhala pakati pa mapewa ake.”

13 Ponena za Yosefe anati:+

“Dziko lake lidalitsidwe ndi Yehova.+

Lidalitsidwe ndi zinthu zabwino kwambiri zakumwamba,

Ndi mame komanso madzi ochokera mu akasupe a pansi pa nthaka.+

14 Lidalitsidwenso ndi zinthu zabwino kwambiri, zochokera ku dzuwa,

Ndi zokolola zabwino kwambiri mwezi uliwonse,+

15 Lidalitsidwe ndi zinthu zabwino koposa zamʼmapiri akale,*+

Ndi zinthu zabwino kwambiri zamʼmapiri amene adzakhalapo mpaka kalekale.

16 Lidalitsidwe ndi zinthu zabwino kwambiri za padziko lapansi, ndi chuma chake chonse,+

Komanso movomerezedwa ndi Iye amene anaonekera mʼchitsamba chaminga.+

Madalitso amenewa akhale pamutu pa Yosefe,

Paliwombo pa munthu amene anasankhidwa pakati pa abale ake.+

17 Ulemerero wake ndi wofanana ndi wa mwana wa ngʼombe wamphongo woyamba kubadwa,

Ndipo nyanga zake ndi nyanga za ngʼombe yamphongo yamʼtchire.

Nyanga zimenezo adzakankha* nazo anthu.

Adzakankha nazo anthu onse pamodzi mpaka kukafika kumalekezero a dziko lapansi.

Nyanga zimenezo ndi anthu masauzande makumimakumi a fuko la Efuraimu,+

Ndiponso anthu masauzande a fuko la Manase.”

18 Ponena za Zebuloni anati:+

“Kondwera Zebuloni iwe, pa maulendo ako,

Ndiponso iwe Isakara, mʼmatenti ako.+

19 Adzaitanira mitundu ya anthu kuphiri.

Kumeneko adzapereka nsembe zachilungamo.

Chifukwa adzatenga chuma* kuchokera pa chuma chochuluka cha mʼnyanja,

Ndi chuma chobisika chamumchenga.”

20 Ponena za Gadi anati:+

“Wofutukula malire a dera la Gadi ndi wodala.+

Iye adzagona kumeneko ngati mkango,

Wokonzeka kukhadzula dzanja, komanso kungʼamba mutu paliwombo.

21 Iye adzasankha gawo labwino kwambiri kuti likhale lake,+

Chifukwa gawo loperekedwa ndi wopereka malamulo linasungidwa kumeneko.+

Atsogoleri a anthu adzasonkhana pamodzi.

Iye adzachita chilungamo cha Yehova,

Ndi zigamulo zake zokhudza Isiraeli.”

22 Ponena za Dani anati:+

“Dani ndi mwana wa mkango.+

Adzadumpha kuchokera ku Basana.”+

23 Ponena za Nafitali anati:+

“Nafitali wakhutira chifukwa chovomerezedwa,

Ndipo madalitso a Yehova amuchulukira.

Tenga chigawo chakumadzulo ndi kumʼmwera.”

24 Ponena za Aseri anati:+

“Aseri anamudalitsa ndi ana aamuna.

Abale ake amukomere mtima,

Ndipo apondetse* mapazi ake mʼmafuta.

25 Chitsulo komanso kopa* ndi zokhomera geti lako,+

Ndipo udzakhala wotetezeka masiku onse a moyo wako.*

26 Palibe amene angafanane ndi Mulungu woona+ wa Yesuruni,+

Amene amayenda mumlengalenga kuti akuthandize,

Amene amayenda pamitambo mu ulemerero wake.+

27 Mulungu ndi malo ako othawirapo kuyambira kalekale,+

Iye wakunyamula mʼmanja ake omwe adzakhalapo mpaka kalekale.+

Adzathamangitsa mdani pamaso pako,+

Ndipo adzanena kuti, ‘Awonongeni!’+

28 Isiraeli adzakhala motetezeka,

Kasupe wa Yakobo adzakhala motetezeka,

Mʼdziko lokhala ndi chakudya komanso vinyo watsopano,+

Limene kumwamba kwake kudzagwetsa mame.+

29 Ndiwe wosangalala iwe Isiraeli!+

Ndani angafanane ndi iwe,+

Anthu amene akupulumutsidwa ndi Yehova,+

Chishango chako chokuteteza,+

Komanso lupanga lako lamphamvu?

Adani ako adzakhala mwamantha chifukwa cha iwe,+

Ndipo iwe udzaponda pamisana yawo.”*

34 Kenako Mose anachoka mʼchipululu cha Mowabu kupita mʼphiri la Nebo,+ pamwamba pa Pisiga,+ moyangʼanizana ndi Yeriko.+ Ndipo Yehova anamuonetsa dziko lonse, kuchokera ku Giliyadi mpaka ku Dani.+ 2 Anamuonetsanso dziko lonse la Nafitali, dziko la Efuraimu, dziko la Manase komanso dziko lonse la Yuda mpaka kunyanja yakumadzulo.*+ 3 Anamuonetsa Negebu+ ndi Chigawo+ cha Yorodano kuphatikizapo chigwa cha Yeriko, mzinda wa mitengo ya kanjedza, mpaka ku Zowari.+

4 Ndiyeno Yehova anamuuza kuti: “Ili ndi dziko limene ndinalumbira kwa Abulahamu, Isaki ndi Yakobo kuti, ‘Ndidzalipereka kwa mbadwa* zanu.’+ Ndakulola kuti ulione ndi maso ako, koma suwoloka kukalowa mʼdzikolo.”+

5 Kenako Mose mtumiki wa Yehova anafera pamenepo mʼdziko la Mowabu, mogwirizana ndi zimene Yehova ananena.+ 6 Mulungu anamuika mʼmanda mʼchigwa, mʼdziko la Mowabu moyangʼanizana ndi Beti-peori, ndipo palibe amene akudziwa pamene pali manda ake mpaka lero.+ 7 Mose anamwalira ali ndi zaka 120.+ Pa nthawiyo maso ake ankaonabe bwinobwino ndipo anali adakali ndi mphamvu. 8 Aisiraeli analira maliro a Mose kwa masiku 30 mʼchipululu cha Mowabu.+ Kenako masiku onse olira maliro a Mose anatha.

9 Yoswa mwana wa Nuni anali atadzazidwa ndi mzimu wa nzeru, chifukwa Mose anaika manja ake pa iye.+ Aisiraeli anayamba kumumvera ndipo anachita mogwirizana ndi zomwe Yehova analamula Mose.+ 10 Koma mu Isiraeli simunakhalenso mneneri aliyense wofanana ndi Mose,+ amene Yehova ankamudziwa bwino kwambiri.*+ 11 Iye anachita zizindikiro ndi zodabwitsa zonse zimene Yehova anamutuma kukachita mʼdziko la Iguputo kwa Farao, atumiki ake onse ndi mʼdziko lake lonse.+ 12 Mose anachita zimenezi ndi dzanja lamphamvu komanso mphamvu zazikulu pamaso pa Aisiraeli onse.+

Mʼchilankhulo choyambirira, “ana a Isiraeli.”

Zikuoneka kuti kumeneku kunali kumapiri a ku Lebanoni.

Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”

Kapena kuti, “kukhwawa la Esikolo.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “achititsa kuti mitima yathu isungunuke.”

Kutanthauza kuti mizindayo inali ndi mipanda italiitali.

Mabaibulo ena amati, “Mulungu wamulimbitsa.”

Kapena kuti, “Musawavutitse.”

Kapena kuti, “khwawa la Zeredi.”

Kapena kuti, “khwawa la Zeredi.”

Kutanthauza Kerete.

Kapena kuti, “khwawa la Arinoni.”

Kapena kuti, “adzamva ululu ngati umene munthu amamva pobereka.”

Kapena kuti, “khwawa la Arinoni.”

Kapena kuti, “khwawa la Yaboki.”

Kapena kuti, “khwawa la Arinoni.”

Kapena kuti, “bokosi limene.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mikono 9.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mikono 4.”

Kapena kuti, “mʼkhwawa la Arinoni.”

Kutanthauza, “Midzi ya Matenti ya Yairi.”

Kapena kuti, “kukhwawa la Arinoni.”

“Kinereti” linali dzina loyambirira la Nyanja ya Galileya.

Imeneyi ndi Nyanja Yakufa.

Kapena kuti, “ndipo musamale moyo wanu.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mpaka mumtima wakumwamba.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Mawu Khumi.”

Kapena kuti, “Musamale moyo wanu.”

Kapena kuti, “cholowa chake.”

Kapena kuti, “mayesero.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”

Kapena kuti, “khwawa la Arinoni.”

Imeneyi ndi Nyanja Yamchere, kapena kuti Nyanja Yakufa.

Kapena kuti, “motsutsana ndi ine.” Mʼchilankhulo choyambirira, “motsutsana ndi nkhope yanga.”

Kapena kuti, “kukoma mtima kosatha.”

Kupha uku ndi kupha munthu mwachiwembu osati mwalamulo.

Mʼchilankhulo choyambirira, “mawu.”

Kapena kuti, “muziwaphunzitsa mobwerezabwereza kuti akhazikike.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “pakati pa maso anu.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “pamaso pa.”

Kapena kuti, “Musamakwatirane ndi anthu a mtundu wina.”

Kapena kuti, “ku mphamvu za Farao.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “adzadalitsa chipatso cha mimba yanu.”

Kapena kuti, “mayesero amphamvu amene.”

Kapena kuti, “makhwawa a madzi.”

“Makangaza” ndi mtundu wa chipatso. Ena amati chimanga chachizungu.

Kapena kuti, “mkuwa.”

Kutanthauza kuti makoma a mipandayo anali ataliatali.

Kapena kuti, “mudzawalande dzikolo.”

Kapena kuti, “fano lopangidwa ndi chitsulo chosungunula.”

Kapena kuti, “chitsulo chosungunula.”

Kapena kuti, “cholowa chanu.”

Kapena kuti, “cholowa chanu.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Mawu Khumi.”

Kapena kuti, “makhwawa a madzi.”

Kapena kuti, “kumwambamwamba.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “muchite mdulidwe wa.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “ndipo musaumitsenso khosi lanu.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”

Kapena kuti, “nʼkumazithirira pogwiritsa ntchito mapazi anu,” mwina popalasa wilo lotungira madzi kapena popanga ndi kutsegula ngalande za madzi.

Mʼchilankhulo choyambirira, “pakati pa maso anu.”

Imeneyi ndi Nyanja Yaikulu ya Mediterranean.

Kapena kuti, “mukalipereke.”

Kapena kuti, “kolowera dzuwa.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Kapena kuti, “gawo limodzi mwa magawo 10.”

Kapena kuti, “zimene akuganiza kuti nʼzabwino.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼmageti anu.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mkati mwa mageti anu onse.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mkati mwa mageti anu.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼmageti anu.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼmageti anu.”

Kapena kuti, “muzimvera mawu a.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “kumeta mpala pachipumi panu.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼmageti anu.”

Kapena kuti, “idzakongola zinthu zanu itakupatsani chikole.”

Kapena kuti, “muzimukongoza atakupatsani chikole.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mtima wanu usamamupatse.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “ngʼombe yamphongo.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼmageti anu.”

Onani Zakumapeto B15.

Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼmageti anu.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼmageti anu onse amene.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Mʼchilankhulo choyambirira, “aziphedwa pakamwa pa.”

Kapena kuti, “mpukutu umene.”

Amenewa ndi malo amene Yehova wasankha kuti akhale malo olambirira.

Mʼchilankhulo choyambirira, “wodutsitsa pamoto mwana wake wamwamuna kapena wamkazi.”

Mawu akuti ‘kuchesulaʼ amatanthauza kupweteka kapena kulepheretsa munthu kuchita chinachake mwa njira ya matsenga.

Mʼchilankhulo choyambirira, “mtima wake ndi wodzaza ndi ukali.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “diso lanu lisamamumvere.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “pakamwa pa.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Diso lanu lisamamve.”

Kapena kuti, “kuchititsa mtima wa abale ake kuti usungunuke ngati wake.”

Kapena kuti, “kukhwawa limene lili.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “ali ndi akazi awiri, mmodzi amamukonda ndipo winayo amadana naye.”

Kapena kuti, “sakumufunanso.”

Kapena kuti, “sakumufunanso.”

Sekeli imodzi inali yofanana ndi magalamu 11.4. Onani Zakumapeto B14.

Kapena kuti, “uhule.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “kuti asavule bambo akewo.”

Kapena kuti, “choipa.”

Chimenechi ndi chimbudzi.

Mʼchilankhulo choyambirira, “galu.”

Kapena kuti, “sakumufunanso.”

Mawu a Chiheberi amene anawamasulira kuti “khate” amatanthauza zambiri kuphatikizapo matenda apakhungu osiyanasiyana opatsirana. Angaphatikizenso matenda ena opezeka mʼzovala ndi mʼnyumba.

Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼmageti anu.”

Kapena kuti, “dzina la nyumba yake.” Mʼchilankhulo choyambirira, “dzina lake.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “ndipo diso lako lisamumvere chisoni.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼnyumba mwanu efa komanso efa.” Onani Zakumapeto B14.

Mʼchilankhulo choyambirira, “zipatso.”

Mabaibulo ena amati, “munthu wa Chiaramu amene watsala pangʼono kufa.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼmageti anu.”

Kutanthauza kukhala pa chisoni chifukwa cha imfa ya munthu amene ankamukonda.

Kapena kuti, “nʼkuipaka laimu woyera.”

Kapena kuti, “mukaipake laimu woyera.”

Kapena kuti, “fano lachitsulo chosungunula nʼkulibisa.”

Kapena kuti, “waluso pa ntchito za matabwa ndi zitsulo.”

Kapena kuti, “Ame!” mʼChiheberi.

Mʼchilankhulo choyambirira, “wavula bambo ake.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Chipatso cha mimba yanu chidzakhala chodalitsika.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Chipatso cha mimba yanu chidzakhala chotembereredwa.”

Mawu a Chiheberi angatanthauzenso kutentha kwa thupi.

Kapena kuti, “mkuwa.”

Matendawa amachititsa kuti munthu atupe kotulukira chimbudzi ndipo nthawi zina amatha kutuluka thumbo.

Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼmageti anu.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “chipatso cha mimba yanu.”

Kapena kuti, “mayesero amphamvu amene.”

Mawu a Chiheberi ali ndi tanthauzo lofanana ndi mawu akuti “ndowe” ndipo amagwiritsidwa ntchito posonyeza kuipidwa.

Mʼchilankhulo choyambirira, “kuti wothiriridwa bwino limodzi ndi wouma.”

Kamzere kameneka kakusonyeza kuti mawuwa anathera mʼmalere.

Kamzere kameneka kakusonyeza kuti mawuwa anathera mʼmalere.

Mʼchilankhulo choyambirira, “mukadzawabweretsanso mumtima mwanu.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “adzachita mdulidwe.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “silili patali.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “kutuluka ndi kulowa.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼmageti anu.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “kugona pamodzi ndi makolo ako.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Muiike mʼkamwa mwawo.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “nʼkunenepa.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “kuuma khosi.”

Mabaibulo ena amati, “mitundu ya anthu.”

Apa akunena Yakobo.

Mʼchilankhulo choyambirira, “mafuta a nkhosa zamphongo.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mafuta apaimpso a tirigu.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “madzi a zipatso za mphesa.”

Kutanthauza “Wolungama.” Limeneli ndi dzina laulemu la Isiraeli.

Kapena kuti, “anandichititsa nsanje.”

Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Mabaibulo ena amati, “wosafuna kumva malangizo.”

Kapena kuti, “imene inkadya nsembe zawo zabwino kwambiri.”

Kapena kuti, “adzayeretsa dziko la anthu ake.”

Dzina lakale la Yoswa. Hoshiya ndi chidule cha dzina lakuti Hoshaiya limene limatanthauza kuti, “Wopulumutsidwa ndi Ya; Ya Wapulumutsa.”

Awa ndi mawu okuluwika otanthauza imfa.

Kapena kuti, “anali ndi oyera ake masauzande masauzande.”

Kutanthauza “Wolungama.” Limeneli ndi dzina laulemu la Isiraeli.

Kapena kuti, “wamenyera nkhondo.”

Mawu akuti “wanu” ndi “inu” akuimira Mulungu.

Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼmphuno mwanu.”

Kapena kuti, “ziuno za.”

Mabaibulo ena amati, “mʼmapiri a kumʼmawa.”

Kapena kuti, “adzagunda.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “adzayamwa chuma chochuluka.”

Kapena kuti, “asambitse.”

Kapena kuti, “mkuwa.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mphamvu zako zidzafanana ndi masiku a moyo wako.”

Mabaibulo ena amati, “pamalo awo okwezeka.”

Imeneyi ndi Nyanja Yaikulu ya Mediterranean.

Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “amene Yehova ankamudziwa pamasomʼpamaso.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena