Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • nwt Acts 1:1-28:31
  • Machitidwe

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Machitidwe
  • Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Machitidwe

MACHITIDWE A ATUMWI

1 A Teofilo, munkhani yoyamba ija, ndinalemba zinthu zonse zimene Yesu anachita ndiponso kuphunzitsa,+ 2 mpaka tsiku limene anatengedwa kupita kumwamba,+ atapereka malangizo kudzera mwa mzimu woyera kwa atumwi amene iye anawasankha.+ 3 Pambuyo pa mavuto amene anakumana nawo, iye anaonekera wamoyo kwa atumwiwo pogwiritsa ntchito maumboni ambiri otsimikizirika.+ Iwo anamuona masiku onse 40 ndipo ankawauza za Ufumu wa Mulungu.+ 4 Pa nthawi imene anasonkhana ndi ophunzirawo, anawapatsa malangizo akuti: “Musachoke mu Yerusalemu,+ koma muyembekezere zimene Atate analonjeza,+ zomwe ndinakuuzani. 5 Chifukwa Yohane ankabatiza ndi madzi, koma inu mudzabatizidwa ndi mzimu woyera+ pasanathe masiku ambiri.”

6 Choncho atasonkhana, anamufunsa kuti: “Ambuye, kodi mubwezeretsa ufumu kwa Aisiraeli panopa?”+ 7 Iye anawayankha kuti: “Simukufunika kudziwa nthawi kapena nyengo imene Atate wasankha mu ulamuliro wake.+ 8 Koma mukadzalandira mzimu woyera, mudzakhala ndi mphamvu.+ Ndipo mudzakhala mboni+ zanga mu Yerusalemu,+ ku Yudeya konse ndi ku Samariya,+ mpaka kumalekezero* a dziko lapansi.”+ 9 Atamaliza kulankhula zimenezi, anatengedwa kupita mumlengalenga iwo akuona, ndipo mtambo unamuphimba moti sanathenso kumuona.+ 10 Pamene iwo ankayangʼanitsitsa kumwamba, iye akukwera kumwambako, mwadzidzidzi azibambo awiri ovala zoyera+ anaima pambali pawo. 11 Azibambowo anawafunsa kuti: “Amuna inu a ku Galileya, nʼchifukwa chiyani mwangoima nʼkumayangʼana kumwamba? Yesu, amene watengedwa pakati panu kupita kumwambayu, adzabwera mʼnjira yofanana ndi mmene mwamuonera akupita kumwamba.”

12 Kenako anabwerera ku Yerusalemu,+ kuchokera kuphiri la Maolivi. Phiri limeneli lili pafupi ndi Yerusalemu, pa mtunda wa ulendo wa tsiku la sabata.* 13 Atafika mumzindawo anapita mʼchipinda chamʼmwamba, mmene ankakhala. Panali Petulo, Yohane, Yakobo, Andireya, Filipo, Tomasi, Batolomeyo, Mateyu, Yakobo mwana wa Alifeyo, Simoni wodzipereka uja komanso Yudasi mwana wa Yakobo.+ 14 Mogwirizana, onsewa ankalimbikira kupemphera pamodzi ndi Mariya mayi a Yesu, azimayi ena+ komanso azichimwene ake a Yesu.+

15 Mʼmasiku amenewa, Petulo anaimirira pakati pa abalewo (gulu lonselo linali la anthu pafupifupi 120) nʼkunena kuti: 16 “Abale anga, zinali zofunika kuti lemba likwaniritsidwe, limene mzimu woyera unaneneratu kudzera mwa Davide. Lembali ndi lokhudza Yudasi,+ amene anatsogolera anthu okagwira Yesu.+ 17 Iye anali mmodzi wa ife,+ ndipo ankatumikira nafe limodzi. 18 (Munthu ameneyu, anagula munda ndi malipiro a ntchito zosalungama.+ Anagwa chamutu nʼkuphulika mimba ndipo matumbo ake onse anakhuthuka.+ 19 Izi zinadziwika kwa anthu onse a ku Yerusalemu, moti munda umenewo anaupatsa dzina la chilankhulo chawo lakuti A·kelʹda·ma, kutanthauza “Munda wa Magazi.”) 20 Mʼbuku la Masalimo analembamo kuti, ‘Malo ake okhala asanduke bwinja, ndipo pasapezeke aliyense wokhalamo,’+ komanso kuti, ‘Udindo wake monga woyangʼanira utengedwe ndi munthu wina.’+ 21 Choncho nʼkofunika kuti alowedwe mʼmalo ndi mmodzi mwa anthu amene ankayenda nafe pa nthawi yonse imene Ambuye Yesu ankachita zinthu zosiyanasiyana pakati pathu. 22 Munthu wake akhale amene ankayenda nafe kuyambira pamene Yesu anabatizidwa ndi Yohane,+ kudzafika tsiku limene anatengedwa kupita kumwamba kuchoka pakati pathu.+ Munthu ameneyu akhale mboni ya kuuka kwa Yesu pamodzi ndi ife.”+

23 Choncho panatchulidwa anthu awiri, Yosefe wotchedwa Barasaba, amene amadziwikanso kuti Yusito, ndi Matiya. 24 Kenako anapemphera kuti: “Inu Yehova,* mumadziwa mitima ya anthu onse,+ tisonyezeni amene mwamusankha pa anthu awiriwa 25 kuti atenge malo amene Yudasi anawasiya nʼkuyenda njira zake ndipo atenge utumikiwu komanso akhale mtumwi.”+ 26 Atatero anachita maere+ ndipo maerewo anagwera Matiya. Choncho iye anamuphatikiza pa atumwi 11 aja.*

2 Tsopano onse anali atasonkhana pamodzi pa tsiku la Chikondwerero cha Pentekosite.+ 2 Mwadzidzidzi, kumwamba kunamveka mkokomo ngati wa mphepo yamphamvu, ndipo phokoso lake linadzaza mʼnyumba yonse imene iwo anali.+ 3 Kenako anaona malilime ooneka ngati malawi amoto, ndipo anagawanika nʼkukhala pa aliyense wa iwo limodzilimodzi. 4 Ndiyeno onsewo anadzazidwa ndi mzimu woyera+ ndipo anayamba kulankhula zilankhulo zosiyanasiyana,* mogwirizana ndi mmene mzimuwo unawachititsira kulankhula.+

5 Pa nthawi imeneyo, Ayuda oopa Mulungu ochokera mʼmitundu yonse yapadziko lapansi ankakhala ku Yerusalemu.+ 6 Choncho mkokomowu utamveka, panasonkhana gulu lalikulu la anthu. Iwo anadabwa kwambiri, chifukwa aliyense anawamva akulankhula mʼchilankhulo chake. 7 Zimenezi zinawadabwitsa kwambiri moti anayamba kufunsana kuti: “Anthuni, kodi onse akulankhulawa si anthu a ku Galileya?+ 8 Ndiye zikutheka bwanji kuti aliyense pagulu lathuli akumva chilankhulo chake? 9 Pano pali Apati, Amedi+ ndi Aelamu.+ Palinso anthu ochokera ku Mesopotamiya, ku Yudeya, ku Kapadokiya, ku Ponto ndi kuchigawo cha Asia.+ 10 Pali anthu ochokera ku Fulugiya, ku Pamfuliya, ku Iguputo ndi kumadera a Libiya amene ali pafupi ndi Kurene. Palinso alendo ochokera ku Roma, omwe ndi Ayuda ndiponso anthu amene analowa Chiyuda.+ 11 Komanso pali Akerete ndi Aluya. Tonsefe tikuwamva akulankhula zinthu zazikulu za Mulungu mʼzilankhulo zathu.” 12 Onse anadabwa kwambiri ndipo anathedwa nzeru moti ankafunsana kuti: “Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani?” 13 Koma ena ankawaseka nʼkumanena kuti: “Aledzera vinyo watsopano amenewa.”

14 Koma Petulo anaimirira pamodzi ndi atumwi 11 aja.+ Iye analankhula nawo mokweza mawu kuti: “Inu anthu a ku Yudeya ndi inu nonse a mu Yerusalemu, dziwani izi ndipo mvetserani mosamala zimene ndikufuna kukuuzani. 15 Sikuti anthuwa aledzera ngati mmene inu mukuganizira, chifukwa nthawi panopa ndi 9 koloko mʼmawa.* 16 Koma zimene zikuchitikazi ndi zimene zinanenedwa kudzera mwa mneneri Yoweli kuti: 17 ‘“Ndipo mʼmasiku otsiriza,” akutero Mulungu, “ndidzapereka* mzimu wanga kwa chamoyo chilichonse, ndipo ana anu aamuna ndi aakazi adzalosera. Anyamata adzaona masomphenya ndipo amuna achikulire adzalota maloto.+ 18 Ngakhale akapolo anga aamuna ndi aakazi, ndidzawapatsa mzimu wanga mʼmasiku amenewo ndipo iwo adzanenera.+ 19 Ndidzachita zodabwitsa kumwamba ndiponso zizindikiro padziko lapansi. Padzakhala magazi, moto ndi utsi wokwera mʼmwamba. 20 Dzuwa lidzasanduka mdima ndipo mwezi udzasanduka magazi. Zimenezi zidzachitika tsiku lalikulu ndiponso laulemerero la Yehova* lisanafike. 21 Ndipo aliyense woitana pa dzina la Yehova* adzapulumuka.”’+

22 Amuna inu a mu Isiraeli, imvani mawu awa: Yesu wa ku Nazareti ndi munthu amene Mulungu anakuonetsani poyera. Anatero kudzera muntchito zamphamvu, zodabwitsa komanso zizindikiro, zimene Mulungu anachita pakati panu kudzera mwa iye,+ ngati mmene inunso mukudziwira. 23 Munthu ameneyu, amene anaperekedwa mwa kufuna kwa Mulungu+ ndi kudziwiratu kwake zamʼtsogolo, munachititsa kuti aphedwe pokhomeredwa pamtengo ndi anthu osamvera malamulo.+ 24 Koma Mulungu anamuukitsa+ pomumasula ku zopweteka* za imfa, chifukwa zinali zosatheka kuti imfa imugwire mwamphamvu.+ 25 Paja Davide ananena za iyeyu kuti, ‘Ndimaika Yehova* patsogolo panga nthawi zonse. Chifukwa iye ali kudzanja langa lamanja, sindidzagwedezeka. 26 Pa chifukwa chimenechi mtima wanga unasangalala ndipo ndinalankhula mosangalala kwambiri. Komanso ine ndidzakhala ndi chiyembekezo, 27 chifukwa simudzandisiya* mʼManda,* ndipo simudzalola kuti thupi la wokhulupirika wanu livunde.*+ 28 Mwandidziwitsa njira za moyo, ndipo mudzachititsa kuti ndizisangalala kwambiri ndikakhala nanu pafupi.’*+

29 Abale anga, ndilankhula ndithu momasuka za kholo lathu Davide. Iye anamwalira nʼkuikidwa mʼmanda,+ ndipo manda ake tili nawo mpaka lero. 30 Iye anali mneneri ndipo ankadziwa kuti Mulungu anamulonjeza polumbira, kuti pampando wake wachifumu adzakhazikapo mmodzi wa mbadwa zake.+ 31 Iye anadziwiratu zamʼtsogolo ndipo ananeneratu za kuuka kwa Khristu kuti sanasiyidwe mʼManda,* komanso thupi lake silinavunde.+ 32 Yesu ameneyo Mulungu anamuukitsa, ndipo tonsefe ndife mboni za nkhani imeneyi.+ 33 Iye anakwezedwa nʼkukhala kudzanja lamanja la Mulungu+ ndipo analandira mzimu woyera wolonjezedwawo kuchokera kwa Atate.+ Choncho iye watipatsa* mzimu woyera umene mukuuona ndi kuumvawu. 34 Ndipotu Davide sanapite kumwamba, koma iyeyo anati, ‘Yehova* anauza Ambuye wanga kuti: “Khala kudzanja langa lamanja 35 mpaka nditaika adani ako kuti akhale chopondapo mapazi ako.”’+ 36 Choncho nyumba yonse ya Isiraeli idziwe ndithu kuti Yesu ameneyu, amene inu munamuphera pamtengo,+ Mulungu anamuika kukhala Ambuye+ ndi Khristu.”

37 Iwo atamva mawu amenewa, anavutika kwambiri mumtima ndipo anafunsa Petulo ndi atumwi enawo kuti: “Abale athu, tichite chiyani pamenepa?” 38 Petulo anawayankha kuti: “Lapani,+ ndipo aliyense abatizidwe+ mʼdzina la Yesu Khristu kuti machimo anu akhululukidwe.+ Mukatero mudzalandira mphatso yaulere ya mzimu woyera. 39 Chifukwa lonjezoli+ laperekedwa kwa inu, kwa ana anu ndiponso kwa anthu onse akutali, onse amene Yehova* Mulungu wathu angawasankhe.”+ 40 Ndipo ndi mawu enanso ambiri, Petulo anachitira umboni mokwanira. Komanso sanaleke kuwadandaulira kuti: “Dzipulumutseni ku mʼbadwo wa maganizo olakwikawu.”+ 41 Choncho amene analandira mawu akewo mosangalala anabatizidwa,+ moti tsiku limenelo chiwerengero cha ophunzirawo chinawonjezereka ndi anthu pafupifupi 3,000.+ 42 Choncho iwo anapitiriza kutsatira zimene atumwiwo ankaphunzitsa, kucheza,* kudyera limodzi+ komanso kupemphera.+

43 Anthu onse anayamba kuchita mantha kwambiri ndipo atumwiwo anayamba kuchita zinthu zodabwitsa ndiponso zizindikiro zambiri.+ 44 Onse amene anakhala okhulupirira ankakhala limodzi ndipo ankagawana zinthu zonse zimene anali nazo. 45 Ankagulitsa malo awo ndi zinthu zina zimene anali nazo+ nʼkugawa kwa onse zimene apeza, mogwirizana ndi zimene aliyense akufunikira.+ 46 Tsiku lililonse ankasonkhana mʼkachisi mogwirizana. Ankaitanirana chakudya mʼnyumba zawo ndiponso ankagawana zakudya mosangalala komanso ndi mtima wonse. 47 Ankatamanda Mulungu ndiponso ankakondedwa ndi anthu onse. Komanso tsiku lililonse, Yehova* anapitiriza kuwonjezera anthu amene ankawapulumutsa.+

3 Tsopano Petulo ndi Yohane ankapita kukalowa mʼkachisi pa nthawi yokapemphera, 3 koloko masana.* 2 Ndiyeno panali mwamuna wina amene anabadwa ali wolumala. Tsiku lililonse ankamunyamula nʼkumukhazika pafupi ndi khomo la kachisi lotchedwa Geti Lokongola, kuti azipempha mphatso zachifundo kwa anthu olowa mʼkachisimo. 3 Munthuyu ataona Petulo ndi Yohane akukalowa mʼkachisimo, anayamba kupempha kuti amupatse mphatso zachifundo. 4 Koma Petulo, pamodzi ndi Yohane, anamuyangʼanitsitsa nʼkunena kuti: “Tiyangʼane.” 5 Iye anawayangʼanitsitsa, akuyembekeza kuti amupatsa kanthu. 6 Koma Petulo anati: “Siliva ndi golide ndilibe, koma ndikupatsa chimene ndili nacho: Mʼdzina la Yesu Khristu wa ku Nazareti, yenda!”+ 7 Atatero anamugwira dzanja lamanja nʼkumuimiritsa.+ Nthawi yomweyo mapazi ndi miyendo* yake zinalimba.+ 8 Zitatero anadumpha nʼkuimirira+ ndipo anayamba kuyenda. Iye analowa nawo limodzi mʼkachisimo, akuyenda, kudumphadumpha komanso kutamanda Mulungu. 9 Anthu onse anamuona akuyenda ndi kutamanda Mulungu. 10 Iwo anamuzindikira kuti ndi munthu amene ankakhala pa Geti Lokongola la kachisi+ nʼkumapempha mphatso zachifundo. Ndipo anthuwo anadabwa kwambiri ndi zimene zinamuchitikirazo.

11 Munthu uja ankangoyendabe ndi Petulo ndi Yohane osawasiya, ndipo gulu lonse la anthu linathamangira kwa iwo pamalo otchedwa Khonde la Zipilala la Solomo,+ likudabwa kwambiri. 12 Petulo ataona zimenezi, anauza anthuwo kuti: “Aisiraeli inu, nʼchifukwa chiyani mukudabwa nazo zimenezi? Nʼchifukwa chiyani mukutiyangʼanitsitsa ngati kuti tamuyendetsa ndi mphamvu zathu kapena chifukwa cha kudzipereka kwathu kwa Mulungu? 13 Mulungu wa Abulahamu, wa Isaki ndi wa Yakobo,+ Mulungu wa makolo athu, ndi amene walemekeza Mtumiki wake+ Yesu,+ amene inu munamupereka+ ndiponso kumukana pamaso pa Pilato, ngakhale kuti Pilatoyo ankafuna kumumasula. 14 Inde, inu munakana woyera ndi wolungamayo, ndipo munapempha kuti akumasulireni munthu wopha anthu.+ 15 Munapha Mtumiki Wamkulu wa moyo,+ koma Mulungu anamuukitsa ndipo ife ndife mboni za nkhani imeneyi.+ 16 Choncho mʼdzina lake komanso chifukwa choti timakhulupirira dzina lakelo, munthu amene mukumuona ndiponso kumudziwayu wachira. Chikhulupiriro chimene ife tili nacho chifukwa cha iye chachititsa kuti achiriretu ngati mmene nonsenu mukuonera. 17 Abale anga, ndikudziwa kuti munachita zinthu mosazindikira,+ ngati mmenenso olamulira anu anachitira.+ 18 Koma pamenepa Mulungu wakwaniritsa zimene analengezeratu kudzera mwa aneneri onse, kuti Khristu wake adzavutika.+

19 Choncho lapani+ ndi kutembenuka+ kuti machimo anu afafanizidwe,+ ndiponso kuti nyengo zotsitsimutsa zibwere kuchokera kwa Yehova.* 20 Komanso kuti atumize Yesu, amene ndi Khristu wosankhidwa chifukwa cha inu. 21 Ameneyu kumwamba kuyenera kumusunga mpaka nthawi yobwezeretsa zinthu zonse, imene Mulungu ananena kudzera mwa aneneri ake oyera akale. 22 Ndipotu Mose ananena kuti, ‘Yehova* Mulungu wanu adzakupatsani mneneri ngati ine kuchokera pakati pa abale anu.+ Mudzamumvere pa zinthu zonse zimene adzakuuzeni.+ 23 Munthu aliyense amene sadzamvera Mneneriyo, Mulungu adzamupha kuti asakhalenso pakati pa anthu.’+ 24 Ndipo aneneri onse, kuyambira pa Samueli mpaka aneneri onse amene anabwera mʼmbuyo mwake, onse amene analosera, ananena mosapita mʼmbali za masiku amenewa.+ 25 Inu ndinu ana a aneneri ndi a pangano limene Mulungu anapangana ndi makolo anu akale.+ Iye anauza Abulahamu kuti: ‘Kudzera mwa mbadwa* yako mabanja onse apadziko lapansi adzadalitsidwa.’+ 26 Mulungu atasankha Mtumiki wake, choyamba+ anamutumiza kwa inu, kuti adzakudalitseni pobweza aliyense wa inu kuti musiye ntchito zanu zoipa.”

4 Pamene Petulo ndi Yohane ankalankhula ndi anthuwo, ansembe, woyangʼanira kachisi ndiponso Asaduki+ anafika. 2 Iwo anakwiya chifukwa atumwiwo ankaphunzitsa anthu ndiponso kulalikira mosapita mʼmbali zoti Yesu anaukitsidwa.+ 3 Choncho anawagwira nʼkuwatsekera mʼndende+ mpaka tsiku lotsatira, chifukwa kunali kutada kale. 4 Koma anthu ambiri amene anamvetsera mawu awo anakhulupirira, ndipo chiwerengero cha amuna chinakwana pafupifupi 5,000.+

5 Tsiku lotsatira, olamulira ndi akulu ndiponso alembi anasonkhana ku Yerusalemu. 6 Panalinso Anasi+ wansembe wamkulu, Kayafa,+ Yohane, Alekizanda ndiponso anthu onse omwe anali achibale a wansembe wamkuluyo. 7 Ndiyeno anaimika Petulo ndi Yohane pakati pawo nʼkuyamba kuwafunsa kuti: “Kodi mphamvu zochitira zimenezi mwazitenga kuti, kapena mwachita izi mʼdzina la ndani?” 8 Petulo, atadzazidwa ndi mzimu woyera,+ anawayankha kuti:

“Inu olamulira ndiponso akulu, 9 ngati lero tikufunsidwa pa zinthu zabwino zimene tachitira munthu wolumalayu+ ndipo mukufuna kudziwa kuti wamuchiritsa ndi ndani, 10 dziwani nonsenu ndi Aisiraeli onse, kuti mʼdzina la Yesu Khristu wa ku Nazareti uja,+ amene inu munamuphera pamtengo,+ koma amene Mulungu anamuukitsa,+ kudzera mwa iyeyo munthuyu waima patsogolo panu ali bwinobwino. 11 Yesu ameneyu ndi ‘mwala umene inu omanga nyumba munauona ngati wopanda pake, umene tsopano wakhala mwala wofunika kwambiri wapakona.’+ 12 Ndiponso palibe munthu aliyense amene angatipulumutse, chifukwa palibe dzina lina+ padziko lapansi limene laperekedwa kwa anthu, lomwe lingatipulumutse.”+

13 Ataona kuti Petulo ndi Yohane akulankhula molimba mtima komanso atakumbukira kuti anali osaphunzira* ndiponso anthu wamba,+ anadabwa kwambiri. Ndipo anazindikira kuti ankayenda ndi Yesu.+ 14 Ndiyeno popeza munthu wochiritsidwa uja anali ataimanso pomwepo,+ iwo anasowa chonena.+ 15 Choncho anawalamula kuti atuluke muholo ya Khoti Lalikulu la Ayuda,* ndipo anayamba kukambirana 16 kuti: “Titani nawo anthu amenewa?+ Chifukwa kunena zoona, iwo achita chizindikiro chachikulu moti anthu onse a ku Yerusalemu aona.+ Ndipo ife sitingatsutse zimenezi. 17 Choncho kuti nkhaniyi isapitirire kufalikira kwa anthu ena, tiyeni tiwaopseze nʼkuwauza kuti asalankhulenso mʼdzina limeneli kwa munthu wina aliyense.”+

18 Atatero anawaitana nʼkuwalamula kuti asalankhulenso kapena kuphunzitsa mʼdzina la Yesu. 19 Koma Petulo ndi Yohane anawayankha kuti: “Weruzani nokha, ngati nʼzoyenera pamaso pa Mulungu kumvera inu mʼmalo momvera Mulunguyo. 20 Koma ife sitingasiye kulankhula za zinthu zimene tinaziona ndi kuzimva.”+ 21 Choncho atawaopsezanso, anawamasula, popeza sanapeze chifukwa chilichonse chowapatsira chilango. Komanso ankaopa anthu,+ poti onse ankatamanda Mulungu chifukwa cha zimene zinachitikazo. 22 Chifukwatu munthu amene anachiritsidwa modabwitsayu anali wazaka zoposa 40.

23 Atawamasula anapita kwa okhulupirira anzawo, ndipo anawafotokozera zonse zimene ansembe aakulu ndi akulu anawauza. 24 Atamva zimenezi, onse pamodzi anafuula kwa Mulungu kuti:

“Ambuye Wamkulu Koposa, inu ndi amene munapanga kumwamba ndi dziko lapansi, nyanja ndi zonse zimene zimakhala mmenemo.+ 25 Pogwiritsa ntchito mzimu woyera, inu munanena kudzera pakamwa pa kholo lathu Davide+ mtumiki wanu kuti, ‘Nʼchifukwa chiyani anthu a mitundu ina akuchita chipolowe ndiponso nʼchifukwa chiyani mitundu ya anthu ikuganizira* zinthu zopanda pake? 26 Mafumu a dziko lapansi anaima pamalo awo, ndipo olamulira anasonkhana mogwirizana kuti alimbane ndi Yehova* komanso wodzozedwa* wake.’+ 27 Zimenezi zinachitikadi pamene Herode, Pontiyo Pilato,+ anthu a mitundu ina komanso anthu a mu Isiraeli, anasonkhana mumzindawu nʼkuukira Yesu, mtumiki wanu woyera, amene inu munamudzoza.+ 28 Anasonkhana kuti achite zimene munaneneratu. Zimenezi zinachitika chifukwa inu muli ndi mphamvu komanso chifukwa zinali zogwirizana ndi chifuniro chanu.+ 29 Koma tsopano Yehova,* imvani mmene akutiopsezera ndipo tithandizeni ife akapolo anu kuti tipitirize kulankhula mawu anu molimba mtima. 30 Pitirizani kuchiritsa anthu ndi dzanja lanu komanso kuthandiza kuti zodabwitsa zipitirize kuchitika+ mʼdzina la Yesu, mtumiki wanu woyera.”+

31 Atamaliza kupemphera mochonderera, malo amene anasonkhanawo anagwedezeka. Kenako onse anadzazidwa ndi mzimu woyera+ ndipo anayamba kulankhula mawu a Mulungu molimba mtima.+

32 Komanso, onse amene anakhulupirira anali ndi maganizo ofanana.* Panalibe aliyense amene ankanena kuti zinthu zimene anali nazo zinali zayekha. Zonse zimene anali nazo zinali za onse.+ 33 Komanso, atumwiwo anapitiriza kuchitira umboni mwamphamvu kwambiri za kuuka kwa Ambuye Yesu.+ Ndipo Mulungu ankawasonyeza onsewo kukoma mtima kwakukulu. 34 Ndipotu panalibe aliyense amene ankasowa kanthu.+ Onse amene anali ndi minda kapena nyumba, ankagulitsa nʼkubweretsa ndalamazo. 35 Ndipo ankazipereka kwa atumwi.+ Ndiyeno ndalamazo ankazigawa kwa aliyense mogwirizana ndi zimene ankafunikira.+ 36 Choncho Yosefe, amene atumwiwo anamupatsa dzina lakuti Baranaba,+ kutanthauza “Mwana Wotonthoza,” amenenso anali Mlevi wobadwira ku Kupuro, 37 anali ndi munda. Iye anagulitsa mundawo nʼkubweretsa ndalamazo kudzazipereka kwa atumwi.+

5 Munthu wina, dzina lake Hananiya, ndi mkazi wake Safira, anagulitsa munda wawo. 2 Koma iye anachotsapo ndalama zina nʼkubisa ndipo mkazi wake anadziwa zimenezo. Ndiyeno anatenga ndalama zotsalazo nʼkukazipereka kwa atumwi.+ 3 Koma Petulo anati: “Hananiya, nʼchifukwa chiyani Satana wakulimbitsa mtima kuti unamize+ mzimu woyera+ nʼkubisa ndalama zina za mundawo? 4 Kodi mundawo sunali mʼmanja mwako usanaugulitse? Ndipo utaugulitsa, ndalamazo sukanatha kuchita nazo zilizonse zimene ukufuna? Ndiye nʼchifukwa chiyani unaganiza zochita zinthu zimenezi? Apatu sunanamize anthu, koma Mulungu.” 5 Hananiya atamva zimenezi anagwa pansi nʼkufa. Ndipo onse amene anamva zimenezi anachita mantha kwambiri. 6 Ndiyeno anyamata anabwera nʼkumukulunga munsalu ndipo anatuluka naye nʼkukamuika mʼmanda.

7 Patapita maola pafupifupi atatu mkazi wake analowa ndipo sankadziwa zimene zachitika. 8 Ndiyeno Petulo anamufunsa kuti: “Tandiuza, kodi ndalama zonse zimene mwapeza mutagulitsa munda wanu ndi izi?” Iye anayankha kuti: “Inde, ndi zomwezo.” 9 Kenako Petulo anamufunsa kuti: “Nʼchifukwa chiyani awirinu munagwirizana kuti muyese mzimu wa Yehova?* Ukudziwa? Anthu amene anapita kukaika mwamuna wako mʼmanda ali pakhomo. Nawenso akunyamula nʼkutuluka nawe.” 10 Nthawi yomweyo Safira anagwa pansi pafupi ndi mapazi a Petulo nʼkufa. Pamene anyamata aja ankalowa anamʼpeza atafa kale. Choncho anamunyamula nʼkutuluka naye ndipo anakamuika mʼmanda pafupi ndi mwamuna wake. 11 Zitatero mpingo wonse ndiponso anthu onse amene anamva zimenezi anachita mantha kwambiri.

12 Atumwiwo anapitiriza kuchita zizindikiro ndiponso zodabwitsa zambiri pakati pa anthu.+ Ndipo okhulupirira onse ankasonkhana Pakhonde la Zipilala la Solomo.+ 13 Nʼzoona kuti palibe aliyense amene analimba mtima kugwirizana ndi ophunzirawo, komabe anthu ankawatamanda kwambiri. 14 Komanso anthu okhulupirira Ambuye anapitiriza kuwonjezereka, chifukwa amuna ndi akazi ambirimbiri anakhala ophunzira.+ 15 Anthuwo ankabweretsa odwala mʼmisewu nʼkuwagoneka pamabedi angʼonoangʼono ndi pamphasa kuti Petulo akamadutsa, chithunzithunzi chake chokha chifike pa ena mwa odwalawo.+ 16 Ndiponso anthu ambiri ochokera mʼmizinda yozungulira Yerusalemu ankapita kumeneko ndi anthu odwala komanso amene mizimu yoipa inkawazunza. Ndipo onsewo ankachiritsidwa.

17 Koma mkulu wa ansembe ndi onse amene anali naye, omwe anali a gulu la mpatuko la Asaduki, anachita nsanje. Choncho iwo ananyamuka 18 nʼkugwira atumwiwo ndipo anawatsekera mʼndende.+ 19 Koma usiku, mngelo wa Yehova* anatsegula zitseko za ndendeyo nʼkuwatulutsa,+ ndipo anawauza kuti: 20 “Pitani mukaime mʼkachisi ndipo mukapitirize kuuza anthu zokhudza moyo umene ukubwerawo.” 21 Atamva zimenezi, mʼmawa kwambiri analowa mʼkachisi nʼkuyamba kuphunzitsa.

Koma mkulu wa ansembe ndi onse amene anali naye anasonkhanitsa Khoti Lalikulu la Ayuda ndiponso akulu onse a Aisiraeli. Kenako anatumiza alonda kundende kuja kuti akatenge atumwiwo nʼkubwera nawo. 22 Koma alonda aja atafika, sanawapeze mʼndendemo. Choncho anabwerera nʼkukanena zimenezi. 23 Iwo anati: “Tapeza ndende ili yokhoma ndiponso yotetezedwa bwino, alonda ataima mʼmakomo. Koma titatsegula sitinapezemo aliyense.” 24 Woyangʼanira kachisi ndi ansembe aakulu atamva zimenezi, anathedwa nzeru chifukwa sankadziwa kuti zitha bwanji. 25 Koma panafika munthu wina nʼkuwauza kuti: “Anthuni! Azibambo munawatsekera mʼndende aja ali mʼkachisi, aima mmenemo ndipo akuphunzitsa anthu.” 26 Zitatero woyangʼanira kachisiyo ananyamuka ndi alonda ake nʼkukawatenga. Koma sanawatenge mwachiwawa, poopa kuponyedwa miyala ndi anthu.+

27 Choncho anabwera nawo nʼkuwaimika muholo ya Khoti Lalikulu la Ayuda. Ndipo mkulu wa ansembe ananena 28 kuti: “Tinakulamulani mwamphamvu kuti musaphunzitsenso mʼdzina limeneli.+ Koma mwadzaza Yerusalemu yense ndi mfundo zimene mukuphunzitsa ndipo mwatsimikiza mtima kuti ife tikhale ndi mlandu wa magazi a munthu ameneyu.”+ 29 Petulo ndi atumwi enawo anayankha kuti: “Ife tiyenera kumvera Mulungu monga wolamulira, osati anthu.+ 30 Mulungu wa makolo athu anaukitsa Yesu, amene inu munamupha pomupachika pamtengo.+ 31 Ndipo Mulungu anamukweza kudzanja lake lamanja+ monga Mtumiki Wamkulu+ ndi Mpulumutsi.+ Anachita zimenezi kuti Aisiraeli alape komanso kuti machimo awo akhululukidwe.+ 32 Ndipo ife ndife mboni za zinthu zimenezi,+ chimodzimodzinso mzimu woyera,+ umene Mulungu wapereka kwa anthu amene amamumvera monga wolamulira.”

33 Atamva zimenezi, anakwiya koopsa moti ankafuna kuwapha. 34 Koma Mfarisi wina dzina lake Gamaliyeli+ anaimirira mʼKhoti Lalikulu la Ayuda. Iyeyu anali mphunzitsi wa Chilamulo wolemekezedwa ndi anthu onse. Ndiyeno analamula kuti anthuwo awatulutse kwakanthawi. 35 Kenako anawauza kuti: “Inu Aisiraeli, musamale ndi zimene mukufuna kuwachita anthu awa. 36 Chifukwa mʼmasiku amʼmbuyomu, kunali Teuda amene anadzitchukitsa kwambiri ndipo anthu pafupifupi 400 analowa mʼgulu lake. Koma anaphedwa, ndipo onse amene ankamutsatira anabalalika, osapezekanso. 37 Kenako kunabwera Yudasi wa ku Galileya mʼmasiku a kalembera. Anthu ambiri anakopeka naye ndipo ankamutsatira. Koma nayenso anafa, ndipo onse amene ankamutsatira anabalalika. 38 Choncho mmene zinthu zilili apapa, ndikukuuzani kuti asiyeni anthu amenewa musalimbane nawo. Chifukwa ngati zolinga zawo kapena ntchito iyi ikuchokera kwa anthu, sipita patali. 39 Koma ngati ikuchokera kwa Mulungu, simungathe kuwaletsa.+ Ndipo mukaumirira mukhoza kupezeka kuti mukulimbana ndi Mulungu.”+ 40 Iwo anamvera malangizo akewa ndipo anaitanitsa atumwiwo. Ndiyeno anangowakwapula*+ nʼkuwalamula kuti asiye kulankhula mʼdzina la Yesu, kenako anawamasula.

41 Zitatero atumwiwo anachoka pamaso pa Khoti Lalikulu la Ayuda. Iwo anali osangalala+ chifukwa Mulungu anawaona kuti ndi oyenera kuchitiridwa chipongwe chifukwa cha dzina la Yesu. 42 Ndipo tsiku lililonse anapitiriza kuphunzitsa mwakhama mʼkachisi ndiponso kunyumba ndi nyumba+ komanso ankalengeza uthenga wabwino wonena za Khristu Yesu.+

6 Pa nthawi imeneyo, pamene ophunzirawo ankapitiriza kuwonjezeka, Ayuda olankhula Chigiriki anayamba kudandaula za Ayuda olankhula Chiheberi. Ankadandaula chifukwa akazi amasiye a Chigiriki ankanyalanyazidwa pa nkhani yogawa chakudya cha tsiku ndi tsiku.+ 2 Choncho atumwi 12 aja anaitana gulu la ophunzira nʼkunena kuti: “Nʼzosayenera kuti ife tisiye ntchito yophunzitsa mawu a Mulungu nʼkuyamba kugawa chakudya.+ 3 Ndiye abale, fufuzani amuna 7 pagulu lanuli a mbiri yabwino,+ amene ali ndi mzimu komanso nzeru,+ kuti ife tiwapatse udindo woyangʼanira ntchito yofunikayi.+ 4 Koma ife tidzipereka pa nkhani yokhudza kupemphera ndiponso kuphunzitsa mawu a Mulungu.” 5 Anthu onsewo anasangalala ndi mawu amenewa moti anasankha Sitefano, munthu wa chikhulupiriro cholimba ndiponso wodzaza ndi mzimu woyera. Anasankhanso Filipo,+ Purokoro, Nikanora, Timoni, Paremena ndi Nikolao wa ku Antiokeya amene analowa Chiyuda. 6 Ndiyeno anawabweretsa kwa atumwi, ndipo atapemphera, atumwiwo anawagwira pamutu* posonyeza kuti awapatsa udindo.+

7 Zitatero mawu a Mulungu anapitiriza kufalikira.+ Chiwerengero cha ophunzira chinkawonjezeka kwambiri+ mu Yerusalemu. Ndipo ansembe ambiri anakhala okhulupirira.+

8 Sitefano anali ndi mphamvu ndipo ankachita kuonekeratu kuti Mulungu ali naye. Iye ankachita zinthu zodabwitsa ndi zizindikiro zazikulu pakati pa anthu. 9 Koma anthu ena a mʼgulu lotchedwa Sunagoge wa Omasulidwa anafika limodzi ndi anthu ena a ku Kurene, a ku Alekizandiriya, ku Kilikiya ndiponso a ku Asia kudzatsutsana ndi Sitefano. 10 Koma iwo sanathe kulimbana ndi nzeru zake komanso mzimu woyera umene unkamutsogolera akamalankhula.+ 11 Kenako ananyengerera amuna ena mwamseri kuti anene kuti: “Tamumva ife ameneyu akulankhula zinthu zonyoza Mose ndi Mulungu.” 12 Zimenezi zinakwiyitsa kwambiri akulu, alembi ndiponso anthu ena. Ndiyeno anabwera modzidzimutsa nʼkumugwira ndipo anapita naye ku Khoti Lalikulu la Ayuda. 13 Iwo anabweretsa mboni zonama, zimene zinanena kuti: “Munthu uyu akungokhalira kulankhula mawu onyoza malo oyerawa ndiponso Chilamulo. 14 Mwachitsanzo, ife tamumva akunena kuti Yesu wa ku Nazareti uja adzawononga malo oyerawa nʼkusintha miyambo imene Mose anatipatsa.”

15 Anthu onse amene anali mʼbwalo la Khoti Lalikulu la Ayuda atayangʼanitsitsa Sitefano, anaona kuti nkhope yake ikuoneka ngati ya mngelo.

7 Koma mkulu wa ansembe anati: “Kodi zimenezi nʼzoona?” 2 Sitefano anati: “Anthu inu, abale anga ndi abambo anga, mvetserani. Mulungu waulemerero anaonekera kwa kholo lathu Abulahamu pamene anali ku Mesopotamiya, asanapite kukakhala ku Harana.+ 3 Ndipo anamuuza kuti, ‘Samuka mʼdziko lako ndipo uchoke pakati pa abale ako. Upite kudziko limene ndidzakuonetse.’+ 4 Choncho anasamuka mʼdziko la Akasidi nʼkukakhala ku Harana. Kumeneko, bambo ake atamwalira,+ Mulungu anamuuza kuti asamukire mʼdziko lino limene inu mukukhala panopa.+ 5 Koma sanamʼpatsemo cholowa chilichonse, ngakhale kadera kakangʼono. Mʼmalomwake anamulonjeza kuti adzamupatsa dzikoli kuti likhale cholowa chake, ndi cha mbadwa* zake,+ ngakhale kuti pa nthawiyo analibe mwana. 6 Ndipo Mulungu anamuuzanso kuti mbadwa* zake zidzakhala alendo mʼdziko la eni, ndipo anthu adzawasandutsa akapolo ndi kuwazunza kwa zaka 400.+ 7 Mulungu anati, ‘Ndidzaweruza mtundu umene adzautumikire monga akapolowo,+ ndipo kenako adzatuluka nʼkudzanditumikira pamalo ano.’+

8 Anamupatsanso pangano la mdulidwe.+ Kenako anabereka Isaki+ ndipo anamudula pa tsiku la 8.+ Nayenso Isaki anabereka* Yakobo ndipo Yakobo anabereka mitu ya mabanja 12 ija. 9 Mitu ya mabanjayo inachitira nsanje Yosefe+ nʼkumugulitsa ku Iguputo.+ Koma Mulungu anali naye,+ 10 ndipo anamupulumutsa mʼmavuto ake onse. Komanso ankamukonda ndipo ankamuthandiza kuti azichita zinthu mwanzeru pamaso pa Farao mfumu ya Iguputo. Faraoyo anapatsa Yosefe udindo woti aziyangʼanira Iguputo ndi nyumba yake yonse.+ 11 Kenako ku Iguputo ndi ku Kanani konse kunagwa njala moti kunali mavuto aakulu. Ndipo makolo athuwo sankapeza chakudya.+ 12 Koma Yakobo anamva kuti ku Iguputo kuli chakudya, ndipo anatuma makolo athu aja kwa nthawi yoyamba.+ 13 Pa ulendo wachiwiri Yosefe anadziulula kwa azichimwene ake, ndipo Farao anadziwa za abale ake a Yosefe ndi makolo ake.+ 14 Choncho Yosefe anatumiza anthu ku Kanani kukatenga bambo ake Yakobo ndiponso abale ake onse.+ Ndipo onse pamodzi analipo anthu 75.+ 15 Ndiyeno Yakobo anapita ku Iguputo+ kumene iye ndi makolo athu aja anafera.+ 16 Kenako mafupa awo anawatenga nʼkupita nawo ku Sekemu. Anakawaika mʼmanda amene Abulahamu anagula ndi ndalama zasiliva kwa ana a Hamori ku Sekemuko.+

17 Nthawi itayandikira, yoti lonjezo limene Mulungu anapereka kwa Abulahamu likwaniritsidwe, mbadwa za Yakobo zinachuluka kwambiri ku Iguputo. 18 Kenako, mfumu ina yomwe sinkadziwa za Yosefe inayamba kulamulira ku Iguputo.+ 19 Mfumu imeneyi inachenjerera anthu a mtundu wathu komanso inakakamiza makolo athuwo kuti azitaya makanda awo nʼcholinga choti asakhale ndi moyo.+ 20 Mose anabadwa pa nthawi imeneyi, ndipo Mulungu ankamuona kuti ndi wokongola. Iye analeredwa mʼnyumba ya bambo ake kwa miyezi itatu.+ 21 Koma pamene anamusiya yekha,+ mwana wamkazi wa Farao anamutenga nʼkumamulera ngati mwana wake.+ 22 Choncho Mose anaphunzira nzeru zonse za Aiguputo. Iye ankalankhula mwamphamvu ndiponso ankachita zinthu zazikulu.+

23 Atakwanitsa zaka 40, anaganiza zokaona* abale ake, Aisiraeli.+ 24 Ataona mmodzi wa abale akewo akuzunzidwa ndi munthu wa ku Iguputo, anamuteteza ndipo anabwezera popha munthu wa ku Iguputoyo. 25 Mose ankaganiza kuti abale akewo azindikira kuti Mulungu akuwapulumutsa pogwiritsa ntchito dzanja lake, koma iwo sanaizindikire mfundo imeneyi. 26 Tsiku lotsatira iye anapitanso kukawaona ndipo anapeza Aisiraeli ena akumenyana. Mose anayesa kuwathandiza kuti agwirizane ponena kuti, ‘Anthu inu, ndinu pachibale. Nʼchifukwa chiyani mukumenyana chonchi?’ 27 Koma amene ankamenya mnzakeyo anamukankha nʼkunena kuti, ‘Ndani anakupatsa udindo woti uzitilamulira komanso kutiweruza? 28 Kodi ukufuna kundipha ngati mmene unaphera munthu wa ku Iguputo dzulo lija?’ 29 Atamva zimenezi, Mose anathawa nʼkukakhala mʼdziko la Midiyani. Kumeneko anabereka ana aamuna awiri.+

30 Patapita zaka 40, mngelo anaonekera kwa iye mʼchipululu paphiri la Sinai, pachitsamba chaminga chimene chinkayaka moto.+ 31 Mose ataona zimenezi, anadabwa kwambiri. Koma pamene ankayandikira kuti aonetsetse, anamva mawu a Yehova* akuti, 32 ‘Ine ndine Mulungu wa makolo ako, Mulungu wa Abulahamu, wa Isaki ndi wa Yakobo.’+ Mose anayamba kunjenjemera ndipo sanafunenso kupita pafupi ndi chitsambacho kuti akaonetsetse. 33 Yehova* anamuuza kuti, ‘Vula nsapato zako, chifukwa malo waimawo ndi malo oyera. 34 Ine ndaona kuti anthu anga omwe ali ku Iguputo akuzunzidwa kwambiri. Ndamva kubuula kwawo+ ndipo ndabwera kudzawapulumutsa. Ndiye ndikufuna ndikutume ku Iguputo.’ 35 Mose yemweyo, amene iwo anamukana nʼkunena kuti, ‘Ndani anakupatsa udindo woti uzitilamulira komanso kutiweruza?’+ ndi amene Mulungu anamutumiza+ ngati wolamulira ndi mpulumutsi kudzera mwa mngelo amene anaonekera kwa iye pachitsamba chaminga chija. 36 Munthu ameneyo anawatsogolera nʼkutuluka nawo+ ndipo anachita zodabwitsa ndi zizindikiro ku Iguputo,+ pa Nyanja Yofiira+ ndiponso mʼchipululu kwa zaka 40.+

37 Ameneyu ndi Mose amene anauza Aisiraeli kuti, ‘Mulungu adzakupatsani mneneri ngati ine, kuchokera pakati pa abale anu.’+ 38 Ameneyu ndi amene anali ndi Aisiraeli mʼchipululu limodzi ndi mngelo+ amene analankhula ndi iyeyu+ komanso makolo athu paphiri la Sinai. Iye analandira mawu opatulika omwe ndi amphamvu kuti atipatsire.+ 39 Koma makolo athu anakana kumumvera. Mʼmalomwake, anamukankhira kumbali+ ndipo mumtima mwawo anabwerera ku Iguputo.+ 40 Anauza Aroni kuti, ‘Tipangire milungu kuti ititsogolere chifukwa sitikudziwa zimene zachitikira Mose, amene ankatitsogolera pochoka ku Iguputo.’+ 41 Choncho iwo anapanga fano la mwana wa ngʼombe mʼmasiku amenewo. Atatero anabweretsa nsembe zopereka kwa fanolo ndipo anasangalala ndi ntchito ya manja awo.+ 42 Choncho Mulungu anawasiya kuti atumikire magulu akumwamba+ ngati mmene malemba amanenera mʼbuku la Aneneri. Malembawo amati, ‘Anthu inu a nyumba ya Isiraeli, kodi mʼchipululu muja munkapereka kwa ine nsembe ndi zopereka zina kwa zaka 40? 43 Inutu munkanyamula chihema cha Moloki+ ndi nyenyezi ya mulungu wotchedwa Refani, mafano amene munapanga kuti muziwalambira. Choncho ndidzakuthamangitsirani kutali kupitirira ku Babulo.’+

44 Makolo athuwo anali ndi chihema cha umboni mʼchipululu. Anachipanga potsatira malangizo amene Mulungu anapereka kwa Mose mogwirizana ndi chithunzi chimene Moseyo anachiona.+ 45 Makolo athu analandira chihemachi kwa makolo awo ndipo analowa nacho limodzi ndi Yoswa mʼdziko limene munali anthu a mitundu ina.+ Anthu amenewa Mulungu anawathamangitsa pamaso pa makolo athu+ ndipo chihemacho chinakhala mʼdzikoli mpaka nthawi ya Davide. 46 Mulungu anakomera mtima Davide ndipo iye anapempha mwayi woti amange nyumba yoti Mulungu wa Yakobo azikhalamo.+ 47 Koma Solomo ndi amene anamangira Mulungu nyumba.+ 48 Komabe Wamʼmwambamwamba sakhala mʼnyumba zomangidwa ndi manja,+ mogwirizana ndi mawu a mneneri akuti, 49 ‘Yehova* wanena kuti, Kumwamba ndi mpando wanga wachifumu+ ndipo dziko lapansi ndi chopondapo mapazi anga.+ Ndiye kodi mungandimangire nyumba yotani? Ndipo malo oti ine ndingapumulirepo ali kuti? 50 Kodi si dzanja langa limene linapanga zinthu zonsezi?’+

51 Anthu okanika inu ndiponso osachita mdulidwe wamumtima ndi mʼmakutu. Nthawi zonse mumatsutsana ndi mzimu woyera. Mukuchita zinthu ngati mmene ankachitira makolo anu.+ 52 Ndi mneneri uti amene makolo anuwo sanamuzunze?+ Iwo anapha anthu amene analengezeratu za kubwera kwa wolungamayo,+ amene inuyo munamupereka ndiponso kumupha.+ 53 Inu munalandira Chilamulo kudzera mwa angelo,+ koma osachitsatira.”

54 Atamva zimenezi, anakwiya koopsa ndipo anayamba kumukukutira mano. 55 Koma iye, atadzazidwa ndi mzimu woyera, anayangʼanitsitsa kumwamba ndipo anaona ulemerero wa Mulungu ndiponso Yesu ataima kudzanja lamanja la Mulungu.+ 56 Ndipo ananena kuti: “Taonani! Ndikuona kumwamba kutatseguka, ndipo Mwana wa munthu+ waima kudzanja lamanja la Mulungu.”+ 57 Iwo atamva zimenezi anafuula kwambiri atatseka mʼmakutu ndi manja awo, ndipo onse anathamangira pamene iye anali. 58 Kenako anamutulutsira kunja kwa mzinda nʼkuyamba kumuponya miyala.+ Ndipo mboni+ zinaika malaya awo akunja pafupi ndi mnyamata wina dzina lake Saulo.+ 59 Pamene ankamuponya miyala, Sitefano anapempha mochonderera kuti: “Ambuye Yesu, landirani mzimu wanga.” 60 Kenako anagwada nʼkufuula ndi mawu amphamvu kuti: “Yehova,* musawaimbe mlandu wa tchimo ili.”+ Atanena zimenezi anafa.*

8 Saulo anavomereza zoti Sitefano aphedwe.+

Tsiku limenelo, mpingo umene unali ku Yerusalemu unayamba kuzunzidwa koopsa. Choncho ophunzira onse, kupatula atumwi okha, anabalalika nʼkupita mʼzigawo za Yudeya ndi Samariya.+ 2 Koma anthu ena oopa Mulungu anatenga Sitefano nʼkukamuika mʼmanda, ndipo anamulira kwambiri. 3 Saulo anayamba kuzunza mpingo mwankhanza. Ankalowa mʼnyumba iliyonse nʼkumakokera panja amuna ndi akazi omwe, ndipo ankawapititsa kundende.+

4 Komabe, anthu amene anabalalika aja ankalalikira uthenga wabwino wa mawu a Mulungu mʼmadera omwe anapita.+ 5 Filipo anapita mumzinda wa Samariya+ nʼkuyamba kulalikira za Khristu kwa anthu akumeneko. 6 Anthu ambiri ankamvetsera zimene Filipo ankanena. Onse ankamvetsera ndiponso kuona zizindikiro zimene iye ankachita. 7 Kumeneko kunali anthu ambiri omwe anali ndi mizimu yoipa ndipo inkafuula nʼkutuluka.+ Anthu ambiri akufa ziwalo ndiponso olumala ankachiritsidwa. 8 Choncho anthu amumzindawo anasangalala kwambiri.

9 Mumzindawo munalinso munthu wina dzina lake Simoni. Izi zisanachitike, iye ankachita zamatsenga nʼkumadabwitsa anthu onse a ku Samariya ndipo ankadzitama kwambiri. 10 Anthu onse, ana ndi akulu omwe, ankachita naye chidwi ndipo ankanena kuti: “Munthu uyu ali ndi mphamvu yaikulu ya Mulungu.” 11 Ankachita naye chidwi chifukwa kwa nthawi yaitali anawadabwitsa ndi zamatsenga zakezo. 12 Koma iwo atakhulupirira Filipo, amene ankalengeza uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu+ ndiponso wonena za dzina la Yesu Khristu, ankabatizidwa, amuna ndi akazi omwe.+ 13 Simoni uja nayenso anakhala wokhulupirira. Atabatizidwa, sankasiyana ndi Filipo+ kulikonse. Moti ankadabwa poona zizindikiro ndiponso ntchito zamphamvu ndi zazikulu zomwe zinkachitika.

14 Atumwi ku Yerusalemu atamva kuti anthu a ku Samariya alandira mawu a Mulungu,+ anawatumizira Petulo ndi Yohane. 15 Iwo anapitadi kumeneko ndipo anawapempherera kuti alandire mzimu woyera.+ 16 Pa nthawiyi nʼkuti aliyense asanalandire mzimu woyera, koma atangobatizidwa mʼdzina la Ambuye Yesu.+ 17 Choncho atumwiwo anayamba kuwagwira anthuwo pamutu,*+ ndipo analandira mzimu woyera.

18 Ndiyeno Simoni ataona kuti atumwiwo akangowagwira anthuwo ankalandira mzimu woyera, anafuna kuwapatsa ndalama. 19 Iye ananena kuti: “Inenso mundipatseko mphamvu imeneyi, kuti aliyense amene ndingamugwire pamutu* azilandira mzimu woyera.” 20 Koma Petulo anamuuza kuti: “Siliva wakoyo uwonongeke naye limodzi, chifukwa ukuganiza kuti mphatso yaulere ya Mulungu ungaigule ndi ndalama.+ 21 Ntchito imeneyi sikukukhudza ndipo ulibe gawo lililonse chifukwa mtima wako si wowongoka pamaso pa Mulungu. 22 Choncho lapa zoipa zimene wachitazi ndipo upemphe Yehova* mochonderera kuti ngati nʼkotheka, akukhululukire chifukwa cha maganizo oipa amene ali mumtima mwakowa. 23 Ndaona kuti ndiwe poizoni wowawa* ndiponso kapolo wa zinthu zachinyengo.” 24 Simoni anayankha kuti: “Ndipempherereni kwa Yehova* mochonderera kuti zonse zimene mwanenazi zisandichitikire.”

25 Choncho atamaliza kuchitira umboni mokwanira ndiponso kulankhula mawu a Yehova,* anabwerera ku Yerusalemu. Pobwerera ankalengeza uthenga wabwino mʼmidzi yambiri ya ku Samariya.+

26 Koma mngelo wa Yehova*+ analankhula kwa Filipo kuti: “Nyamuka ndipo upite kumʼmwera, kumsewu wochokera ku Yerusalemu kupita ku Gaza.” (Umenewu ndi msewu wa mʼchipululu.) 27 Choncho, ananyamuka nʼkupita ndipo anakumana ndi nduna ya ku Itiyopiya. Munthuyu anali ndi udindo waukulu ndipo ankathandiza Kandake, mfumukazi ya Itiyopiya. Ankayangʼaniranso chuma chonse cha mfumukaziyo. Iye anapita ku Yerusalemu kukalambira Mulungu.+ 28 Tsopano anali pa ulendo wobwerera kwawo atakhala mʼgaleta lake ndipo ankawerenga mokweza ulosi wa mneneri Yesaya. 29 Ndiyeno mzimu unauza Filipo kuti: “Pita ukayandikire galeta lakelo.” 30 Filipo anathamanga nʼkumayenda mʼmbali mwa galetalo ndipo anamumva akuwerenga mokweza ulosi wa mneneri Yesaya. Filipo anamufunsa kuti: “Kodi mukumvetsa zimene mukuwerengazo?” 31 Iye anayankha kuti: “Ndingamvetse bwanji popanda wondimasulira?” Choncho anapempha Filipo kuti akwere nʼkukhala naye mʼgaletamo. 32 Mawu a mʼMalemba amene ankawerengawo anali akuti: “Anamutengera kumalo oti akamuphere ngati nkhosa. Ndipo mofanana ndi mwana wa nkhosa amene wangokhala chete pamene akufuna kumumeta ubweya, sanatsegule pakamwa pake.+ 33 Pamene ankamuchititsa manyazi, sanamuchitire zachilungamo.+ Ndi ndani angafotokoze mwatsatanetsatane mʼbadwo wa makolo ake? Chifukwa moyo wake wachotsedwa padziko lapansi.”+

34 Ndiyeno ndunayo inafunsa Filipo kuti: “Ndiuzeni chonde, kodi mneneriyu akunena za ndani? Za iyeyo kapena za munthu wina?” 35 Zitatero, Filipo anayamba kumuuza uthenga wabwino wonena za Yesu, ndipo anayambira palemba lomweli. 36 Akuyenda choncho mumsewumo, anapeza madzi ambiri ndipo nduna ija inati: “Taonani, Madzitu awo! Chikundiletsa kubatizidwa nʼchiyani?” 37*⁠—— 38 Atatero analamula kuti galetalo liime. Kenako Filipo ndi nduna ija anatsika nʼkulowa mʼmadzimo, ndipo Filipo anabatiza ndunayo. 39 Atatuluka mʼmadzimo mzimu wa Yehova* unamuchotsapo Filipo mwamsanga ndipo nduna ija sinamuonenso, koma inapitiriza ulendo wake ikusangalala. 40 Koma Filipo anapezeka ali ku Asidodi, ndipo anayamba kulengeza uthenga wabwino mʼmizinda yonse yamʼderali mpaka anakafika ku Kaisareya.+

9 Koma Saulo anapitiriza kuopseza ophunzira a Ambuye+ komanso ankafunitsitsa kuwapha. Choncho anapita kwa mkulu wa ansembe 2 kukapempha makalata a chilolezo kuti apite nawo kumasunagoge a ku Damasiko. Anapempha makalatawo kuti akakapeza wina aliyense wotsatira Njirayo,*+ mwamuna kapena mkazi, akamumange nʼkubwera naye ku Yerusalemu.

3 Ali pa ulendo wakewo, atatsala pangʼono kufika ku Damasiko, mwadzidzidzi anangoona kuwala kochokera kumwamba kutamuzungulira.+ 4 Zitatero anagwa pansi ndipo anamva mawu akuti: “Saulo, Saulo, nʼchifukwa chiyani ukundizunza?” 5 Iye anafunsa kuti: “Mbuyanga, ndinu ndani kodi?” Anamuyankha kuti: “Ndine Yesu,+ amene ukumuzunza.+ 6 Nyamuka, ulowe mumzindawo, ndipo ukauzidwa zoyenera kuchita.” 7 Anthu amene anali naye limodzi pa ulendowo, anangoima kusowa chonena. Iwo anamva ndithu kuti munthu akulankhula, koma sanaone aliyense.+ 8 Kenako Saulo anaimirira, koma ngakhale kuti ankayangʼana, sankaona chilichonse. Choncho anamugwira dzanja nʼkumulondolera ku Damasiko. 9 Saulo anakhala masiku atatu asakuona+ ndipo sanadye kapena kumwa chilichonse.

10 Ku Damasiko kunali wophunzira wina dzina lake Hananiya.+ Ndiyeno Ambuye analankhula naye mʼmasomphenya kuti: “Hananiya!” Iye anayankha kuti: “Ine Ambuye.” 11 Kenako Ambuyewo anamuuza kuti: “Nyamuka upite ku Msewu Wowongoka. Ukakafika panyumba ya Yudasi, ukafunse za munthu wina dzina lake Saulo, wa ku Tariso.+ Iyeyo akupemphera, 12 ndipo mʼmasomphenya waona munthu dzina lake Hananiya atafika nʼkumugwira pamutu* kuti ayambenso kuona.”+ 13 Koma Hananiya anayankha kuti: “Ambuye, ndamva kwa anthu ambiri za munthu ameneyu. Ndamva zoipa zonse zimene anachitira oyera anu ku Yerusalemu. 14 Ndipo panopa ansembe aakulu amupatsa mphamvu kuti amange onse oitana pa dzina lanu.”+ 15 Koma Ambuye anamuuza kuti: “Pita, chifukwa munthu ameneyu ndi chiwiya changa+ chosankhidwa chotengera dzina langa kupita nalo kwa anthu a mitundu ina+ komanso kwa mafumu+ ndi Aisiraeli. 16 Popeza ndidzamuonetsa bwinobwino mavuto onse amene adzakumane nawo chifukwa cha dzina langa.”+

17 Choncho Hananiya anapita nʼkukalowa mʼnyumbamo. Ndiyeno anamugwira pamutu* nʼkunena kuti: “Mʼbale wanga Saulo, Ambuye Yesu amene anaonekera kwa iwe pamsewu umene unadzera, wandituma. Wandituma kwa iwe kuti uyambenso kuona komanso udzazidwe ndi mzimu woyera.”+ 18 Nthawi yomweyo tinthu tooneka ngati mamba a nsomba tinagwa kuchokera mʼmaso mwa Saulo ndipo anayambanso kuona. Kenako anapita kukabatizidwa. 19 Atadya chakudya anapezanso mphamvu.

Iye anakhala ndi ophunzira ku Damasiko kwa masiku angapo.+ 20 Nthawi yomweyo anayamba kulalikira za Yesu mʼmasunagoge, kuti ameneyu ndi Mwana wa Mulungu. 21 Koma anthu onse amene anamumva akulankhula, anadabwa kwambiri ndipo ankanena kuti: “Kodi munthu uyu si uja ankazunza anthu a ku Yerusalemu oitana pa dzina limeneli?+ Kodi chimene anabwerera kuno si kudzagwira anthu nʼkupita nawo kwa ansembe aakulu?”+ 22 Komabe Saulo anapitiriza kukhala ndi mphamvu zambiri ndipo ankathetsa nzeru Ayuda a ku Damasiko powafotokozera mfundo zomveka zotsimikizira kuti Yesu ndi Khristu.+

23 Patapita masiku ambiri, Ayudawo anakonza chiwembu choti amuphe.+ 24 Koma Saulo anadziwa za chiwembucho. Iwo ankayangʼananso mosamala mʼmageti masana onse ndiponso usiku kuti amuphe. 25 Choncho usiku, ophunzira ake anamuika mʼdengu nʼkumutulutsira pawindo la mpanda nʼkumutsitsira kunja.+

26 Atafika ku Yerusalemu+ anayesetsa kuti agwirizane ndi ophunzira kumeneko. Koma onse ankamuopa, chifukwa sankakhulupirira kuti ndi wophunzira. 27 Choncho Baranaba+ anamuthandiza popita naye kwa atumwi. Ndipo anawafotokozera mwatsatanetsatane mmene Saulo anaonera Ambuye+ amene analankhula naye pamsewu. Anawafotokozeranso mmene Saulo analankhulira molimba mtima ku Damasiko mʼdzina la Yesu.+ 28 Zitatero anapitiriza kukhala nawo nʼkumayenda momasuka mu Yerusalemu, ndipo ankalankhula molimba mtima mʼdzina la Ambuye. 29 Iye ankalankhulana ndiponso kutsutsana ndi Ayuda olankhula Chigiriki. Koma iwo anayamba kufufuza njira yoti amuphere.+ 30 Abale atazindikira zimenezi, anapita naye ku Kaisareya nʼkumutumiza ku Tariso.+

31 Ndiyeno mpingo ku Yudeya konse, ku Galileya ndi ku Samariya+ unayamba kukhala pamtendere ndipo unali wolimba. Chifukwa choti ophunzira ankaopa Yehova* komanso ankalimbikitsidwa ndi mzimu woyera,+ mpingowo unkakulirakulira.

32 Pamene Petulo ankayenda mʼdera lonselo, anafikanso kwa oyera amene ankakhala ku Luda.+ 33 Kumeneko anapeza munthu wina dzina lake Eneya, yemwe anakhala chigonere pabedi lake kwa zaka 8 chifukwa anali wakufa ziwalo. 34 Ndiyeno Petulo anamuuza kuti: “Eneya, Yesu Khristu akukuchiritsa.+ Dzuka ndipo ukonze pabedi lakolo.”+ Nthawi yomweyo anadzuka. 35 Anthu onse a ku Luda ndiponso kuchigwa cha Sharoni atamuona, anayamba kukhulupirira Ambuye.

36 Ku Yopa kunali wophunzira wina dzina lake Tabita, dzina limene limamasuliridwa kuti Dorika.* Tabita ankachita zinthu zambiri zabwino ndiponso ankapatsa ena mphatso zambiri zachifundo. 37 Ndiyeno mʼmasiku amenewo iye anadwala ndipo anamwalira. Choncho anamusambitsa nʼkukamugoneka mʼchipinda chamʼmwamba. 38 Popeza kuti Luda anali pafupi ndi Yopa, ophunzirawo atamva kuti Petulo ali mumzindawu, anatuma anthu awiri kukamupempha kuti: “Chonde mubwere kwathu mwamsanga.” 39 Petulo atamva zimenezi, ananyamuka nʼkupita nawo limodzi. Atafika, anamutenga nʼkupita naye mʼchipinda chamʼmwamba chija. Akazi onse amasiye anabwera kwa iye akulira ndipo ankamuonetsa zovala zambiri ndiponso mikanjo imene Dorika ankasoka pamene anali nawo. 40 Petulo anauza anthu onse kuti atuluke,+ ndiyeno anagwada nʼkupemphera. Kenako anatembenuka nʼkuyangʼana mtembowo nʼkunena kuti: “Tabita, dzuka!” Ndiyeno mayiyo anatsegula maso ndipo ataona Petulo, anadzuka nʼkukhala tsonga.+ 41 Petulo anamugwira dzanja nʼkumuimiritsa. Atatero anaitana oyerawo komanso akazi amasiye aja, ndipo onse anaona kuti Tabita ali moyo.+ 42 Izi zinadziwika ku Yopa konse ndipo anthu ambiri anakhulupirira Ambuye.+ 43 Petulo anakhalabe ku Yopa kwa masiku angapo ndipo ankakhala kwa munthu wina wofufuta zikopa, dzina lake Simoni.+

10 Ku Kaisareya kunali munthu wina dzina lake Koneliyo, mtsogoleri wa asilikali* a mʼgulu la asilikali a ku Italy.* 2 Iyeyu ankakonda zopemphera ndipo ankaopa Mulungu pamodzi ndi banja lake lonse. Komanso ankapatsa anthu mphatso zachifundo zambiri ndipo ankapemphera mochonderera kwa Mulungu nthawi zonse. 3 Tsiku lina cha mʼma 3 koloko+ masana,* anaona masomphenya. Mngelo wa Mulungu anabwera kwa iye nʼkunena kuti: “Koneliyo!” 4 Zitatero, Koneliyo anayangʼanitsitsa mngeloyo mwamantha nʼkunena kuti: “Lankhulani Mbuyanga.” Mngeloyo anamuuza kuti: “Mulungu wamva mapemphero ako ndiponso waona mphatso zako zachifundo.+ 5 Choncho tumiza anthu ku Yopa kuti akaitane munthu wina dzina lake Simoni, wotchedwanso Petulo. 6 Munthu ameneyu ndi mlendo kunyumba kwa Simoni wina wofufuta zikopa, amene nyumba yake ili mʼmbali mwa nyanja.” 7 Mngelo amene ankalankhula nayeyo atangochoka, Koneliyo anaitana atumiki ake awiri ndiponso msilikali wake wina amene ankakonda zopemphera. 8 Iye anawafotokozera zonse nʼkuwatuma ku Yopa.

9 Tsiku lotsatira, ulendo wawo uli mkati komanso akuyandikira mzindawo, Petulo anakwera padenga kukapemphera cha mʼma 12 koloko masana.* 10 Koma anamva njala kwambiri ndipo ankafuna kudya. Pamene chakudya chinkakonzedwa, anayamba kuona masomphenya.+ 11 Mʼmasomphenyawo anaona kumwamba kutatseguka, chinthu chinachake chooneka ngati chinsalu chachikulu chikutsika. Chinthucho anachigwira mʼmakona onse 4 nʼkumachitsitsira padziko lapansi. 12 Pachinthucho panali mitundu yonse ya nyama za miyendo 4, nyama zokwawa zapadziko lapansi ndiponso mbalame zamumlengalenga. 13 Kenako anamva mawu akuti: “Petulo, nyamuka ndipo uphe zinthu zimenezi nʼkudya.” 14 Koma Petulo anati: “Ayi Ambuye, ine sindinadyepo chinthu chodetsedwa ndiponso chonyansa chilichonse.”+ 15 Koma anamvanso mawu aja kachiwiri kuti: “Zinthu zimene Mulungu waziyeretsa, usiyiretu kunena kuti nʼzodetsedwa.” 16 Anamvanso mawu amenewa kachitatu, ndipo nthawi yomweyo chinthu chooneka ngati chinsalu chija chinatengedwa kupita kumwamba.

17 Petulo atathedwa nzeru chifukwa chosamvetsa tanthauzo la masomphenyawo, anthu amene Koneliyo anawatuma aja anafunsa kuti nyumba ya Simoni ili kuti ndipo anali ataima pageti.+ 18 Iwo anafunsa mofuula ngati kumeneko anali ndi mlendo dzina lake Simoni wotchedwanso Petulo. 19 Petulo akuganizirabe za masomphenyawo, mzimu wa Mulungu+ unamuuza kuti: “Petulo! Pali anthu atatu amene akukufuna. 20 Ndiye konzeka, tsika upite nawo limodzi. Usakayikire, chifukwa ndawatuma ndine.” 21 Choncho Petulo anatsika nʼkukakumana ndi anthuwo ndipo anati: “Amene mukumufunayo ndine. Tikuthandizeni?” 22 Iwo anati: “Tachokera kwa Koneliyo,+ mtsogoleri wa asilikali. Iye ndi munthu wolungama komanso woopa Mulungu ndipo mtundu wonse wa Ayuda umamuyamikira. Mngelo woyera anamupatsa malangizo ochokera kwa Mulungu kuti atume anthu kudzakutengani kuti mupite kunyumba kwake, akamve zimene inu mukanene.” 23 Ndiyeno anawalowetsa mʼnyumba nʼkuwasamalira monga alendo ake.

Kutacha, ananyamuka nʼkupita nawo ndipo abale ena a ku Yopa anapita naye limodzi. 24 Tsiku lotsatira anafika ku Kaisareya ndipo Koneliyo ankawayembekezeradi. Iye anali atasonkhanitsa achibale ake ndi anzake apamtima. 25 Petulo akulowa, Koneliyo anakumana naye ndipo anagwada posonyeza kumulambira. 26 Koma Petulo anamudzutsa nʼkunena kuti: “Imirira, inenso ndine munthu ngati iwe wemwe.”+ 27 Kenako analowa mkati uku akukambirana ndipo anapeza anthu ambiri atasonkhana. 28 Ndiyeno Petulo anawauza kuti: “Inunso mukudziwa bwino kuti si zololeka kuti Myuda azicheza ndi munthu wa mtundu wina kapena kumuyandikira.+ Koma Mulungu wandionetsa kuti ndisatchule munthu aliyense kuti wodetsedwa kapena wonyansa.+ 29 Nʼchifukwa chake ndabwera mosanyinyirika mutatumiza anthu kuti adzandiitane. Choncho ndiuzeni chimene mwandiitanira.”

30 Ndiyeno Koneliyo anati: “Masiku 4 apitawo, ine ndikupemphera mʼnyumba mwanga muno cha mʼma 3 koloko masana,* ndinangoona munthu wovala zowala ataima kutsogolo kwanga. 31 Munthuyo anandiuza kuti, ‘Koneliyo, Mulungu wamva pemphero lako ndiponso waona mphatso zako zachifundo. 32 Choncho tumiza anthu ku Yopa kuti akaitane Simoni wotchedwanso Petulo. Munthu ameneyo ndi mlendo mʼnyumba ya Simoni wofufuta zikopa, amene amakhala mʼmbali mwa nyanja.’+ 33 Nthawi yomweyo ndinatuma anthu kuti akakuitaneni ndipo mwatikomera mtima nʼkubwera. Choncho tonse tili pano pamaso pa Mulungu, kuti timve zonse zimene Yehova* wakulamulani kuti mutiuze.”

34 Petulo atamva zimenezi, anayamba kulankhula kuti: “Ndazindikira ndithu kuti Mulungu alibe tsankho.+ 35 Iye amalandira munthu wochokera mu mtundu uliwonse, amene amamuopa ndi kuchita chilungamo.+ 36 Mulungu anatumiza mawu kwa Aisiraeli nʼkulengeza kwa iwo uthenga wabwino wa mtendere+ kudzera mwa Yesu Khristu. Ameneyu ndi Ambuye wa onse.+ 37 Inu mukudziwa nkhani imene inali mʼkamwamʼkamwa kuyambira ku Galileya+ mpaka ku Yudeya konse, pambuyo pa ubatizo umene Yohane ankalalikira. 38 Nkhani yake inali yonena za Yesu wa ku Nazareti, amene Mulungu anamudzoza ndi mzimu woyera+ ndi mphamvu. Popeza Mulungu anali naye,+ anayenda mʼdziko lonse nʼkumachita zabwino ndiponso kuchiritsa anthu onse amene Mdyerekezi+ ankawazunza. 39 Ndipo ife ndife mboni za zinthu zonse zimene anachita mʼdziko la Ayuda ndi ku Yerusalemu komwe. Koma Aisiraeliwo anamupha pomupachika pamtengo. 40 Ameneyu Mulungu anamuukitsa pa tsiku lachitatu+ nʼkulola kuti anthu amuone, 41 osati anthu onse, koma mboni zimene Mulungu anasankhiratu, zomwe ndi ifeyo, amene tinadya ndiponso kumwa naye limodzi ataukitsidwa.+ 42 Ndiponso, anatilamula kuti tilalikire kwa anthu ndi kupereka umboni wokwanira+ woti iyeyu ndi amene Mulungu anamupatsa udindo woweruza anthu amoyo ndi akufa.+ 43 Aneneri onse amachitira umboni za iyeyu,+ kuti aliyense womukhulupirira, machimo ake amakhululukidwa mʼdzina lake.”+

44 Pamene Petulo ankalankhula zimenezi, anthu onse amene ankamvetsera mawuwo analandira mzimu woyera.+ 45 Ndipo okhulupirira amene anabwera ndi Petulo aja, amenenso anali odulidwa, anadabwa kwambiri. Iwo anadabwa chifukwa mphatso yaulere ya mzimu woyera inaperekedwanso kwa anthu a mitundu ina. 46 Chifukwanso anawamva akulankhula zilankhulo zina* ndiponso kulemekeza Mulungu.+ Ndiyeno Petulo anati: 47 “Anthu awa alandira mzimu woyera ngati mmenenso ife tinalandirira. Ndani amene angaletse kuti asabatizidwe mʼmadzi?”+ 48 Atatero anawalamula kuti abatizidwe mʼdzina la Yesu Khristu.+ Ndiyeno iwo anamupempha kuti akhalebe nawo kwa masiku angapo.

11 Tsopano atumwi ndi abale amene anali ku Yudeya anamva kuti anthu a mitundu ina nawonso alandira mawu a Mulungu. 2 Koma Petulo atapita ku Yerusalemu, anthu olimbikitsa mdulidwe+ anayamba kumuimba mlandu. 3 Iwo ankamunena kuti: “Iwe unakalowa mʼnyumba ya anthu osadulidwa ndipo unadya nawo.” 4 Ndiyeno Petulo anayamba kuwafotokozera mwatsatanetsatane zimene zinachitika kuti:

5 “Ine ndikupemphera mumzinda wa Yopa, ndinaona masomphenya. Ndinaona chinthu chooneka ngati chinsalu chachikulu chikutsika kuchokera kumwamba. Chinthucho anachigwira mʼmakona onse 4 nʼkuchitsitsira pamene ndinali.+ 6 Nditachiyangʼanitsitsa, ndinaonamo nyama za miyendo 4 zapadziko lapansi, nyama zakutchire, nyama zokwawa komanso mbalame zamumlengalenga. 7 Ndinamvanso mawu akuti: ‘Petulo, nyamuka ndipo uphe zinthu zimenezi nʼkudya.’ 8 Koma ine ndinati, ‘Ayi Ambuye, mʼkamwa mwanga simunalowepo chinthu chilichonse chodetsedwa ndiponso chonyansa.’ 9 Koma ndinamvanso mawu aja kachiwiri kuti: ‘Zinthu zimene Mulungu waziyeretsa, usiyiretu kunena kuti nʼzodetsedwa.’ 10 Mawuwo anamvekanso kachitatu, ndipo kenako zonse zija zinatengedwa kupita kumwamba. 11 Nthawi yomweyo, anthu atatu amene anatumidwa kwa ine kuchokera ku Kaisareya anaima panyumba imene tinkakhala.+ 12 Kenako mzimu unandiuza kuti ndipite nawo, ndisakayikire ngakhale pangʼono. Abale 6 awa anapita nane limodzi ndipo tinakalowa mʼnyumba ya munthuyo.

13 Iye anatiuza kuti ali mʼnyumba mwake anaona mngelo ataimirira ndipo anamuuza kuti, ‘Tuma anthu kuti apite ku Yopa akaitane Simoni wotchedwanso Petulo.+ 14 Iye adzakuuza zinthu zimene zidzathandize iweyo ndi anthu onse a mʼbanja lako kupulumuka.’ 15 Koma nditangoyamba kulankhula, iwo analandira mzimu woyera ngati mmene zinalilinso ndi ifeyo poyamba paja.+ 16 Zitatero ndinakumbukira mawu amene Ambuye ankakonda kunena aja akuti, ‘Yohane ankabatiza ndi madzi,+ koma inu mudzabatizidwa ndi mzimu woyera.’+ 17 Choncho ngati Mulungu anawapatsa mphatso yaulere yomwenso anatipatsa ifeyo amene tinakhulupirira mwa Ambuye Yesu Khristu, ndine ndani kuti ndiletse Mulungu?”+

18 Atamva zimenezi, anasiya kumutsutsa,* ndipo anatamanda Mulungu kuti: “Ndiye kuti Mulungu waperekanso mwayi kwa anthu a mitundu ina kuti nawonso alape nʼkudzapeza moyo.”+

19 Anthu amene anabalalika+ chifukwa cha mavuto amene anayamba chifukwa cha zimene zinachitikira Sitefano, anakafika mpaka ku Foinike, ku Kupuro ndi ku Antiokeya. Ndipo ankangolalikira kwa Ayuda okha.+ 20 Koma ena mwa anthuwa anali a ku Kupuro ndi ku Kurene. Iwowa atafika ku Antiokeya anayamba kulengeza uthenga wabwino wa Ambuye Yesu kwa anthu olankhula Chigiriki. 21 Dzanja la Yehova* linkawathandiza ndipo anthu ambiri anakhulupirira nʼkuyamba kutsatira Ambuye.+

22 Mpingo wa ku Yerusalemu unamva za anthuwa ndipo unatumiza Baranaba+ kuti apite ku Antiokeya. 23 Atafika kumeneko nʼkuona kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu, anasangalala ndipo anayamba kulimbikitsa onse kuti apitirize ndi mtima wonse kukhala okhulupirika kwa Ambuye.+ 24 Baranaba anali munthu wabwino komanso wa chikhulupiriro cholimba. Iye ankatsogoleredwa kwambiri ndi mzimu woyera ndipo anthu enanso ambiri anakhulupirira Ambuye.+ 25 Kenako Baranaba anapita ku Tariso kukafufuza Saulo.+ 26 Atamupeza anabwera naye ku Antiokeya. Iwo anasonkhana ndi mpingo kumeneko kwa chaka chathunthu ndipo anaphunzitsa anthu ambiri. Ku Antiokeya nʼkumene ophunzirawo anayamba kutchedwa Akhristu, motsogoleredwa ndi Mulungu.+

27 Pa nthawiyi, aneneri+ ochokera ku Yerusalemu anapita ku Antiokeya. 28 Mothandizidwa ndi mzimu wa Mulungu, mmodzi wa iwo dzina lake Agabo,+ analosera kuti padziko lonse lapansi+ padzagwa njala yaikulu. Izi zinachitikadi mʼnthawi ya Kalaudiyo. 29 Choncho ophunzirawo anatsimikiza mtima kutumiza thandizo+ kwa abale a ku Yudeya, aliyense mogwirizana ndi zimene akanakwanitsa.+ 30 Ndipo anachitadi zimenezo moti thandizolo anapatsira Baranaba ndi Saulo kuti akapereke kwa akulu.+

12 Pa nthawi imeneyi Mfumu Herode* anayamba kuzunza anthu ena amumpingo.+ 2 Iye anapha ndi lupanga+ Yakobo, mchimwene wake wa Yohane.+ 3 Ataona kuti zimenezi zasangalatsa Ayuda, anamanganso Petulo. (Anamumanga mʼmasiku a Mikate Yopanda Zofufumitsa.)+ 4 Anamugwira nʼkumutsekera mʼndende+ ndipo anamusiya mʼmanja mwa magulu 4 a asilikali kuti azisinthana pomulondera. Gulu lililonse linali ndi asilikali 4. Cholinga cha Herode chinali chakuti adzamuzenge mlandu pamaso pa anthu Pasika akatha. 5 Choncho Petulo anatsekeredwa mʼndendemo, koma mpingo unkamupempherera kwambiri kwa Mulungu.+

6 Pamene Herode ankakonza zoti abweretse Petulo kwa anthu, usiku umenewo Petuloyo anagona pakati pa asilikali awiri atamumanga ndi maunyolo awiri. Pakhomo panalinso alonda omwe ankalondera ndendeyo. 7 Koma mwadzidzidzi, mngelo wa Yehova* anafika,+ ndipo mʼchipinda cha ndendeyo munawala. Kenako mngeloyo anadzutsa Petulo pomugwedeza mʼnthiti nʼkunena kuti: “Dzuka msanga!” Atatero maunyolo amene anamumanga nawo manjawo anagwa pansi.+ 8 Mngeloyo anamuuza kuti: “Vala zovala zako ndi nsapato zako.” Iye anachitadi zimenezo. Kenako anamuuza kuti: “Vala malaya ako akunja ndipo uzinditsatira.” 9 Iye anatuluka nʼkumamutsatira, koma sanadziwe kuti zimene zinkachitika ndi mngelozo zinalidi zenizeni. Ankangoganiza kuti akuona masomphenya. 10 Atapitirira gulu loyamba la asilikali apageti ndi lachiwiri, anafika pageti lachitsulo lotulukira popita mumzinda, ndipo linatseguka lokha. Atatuluka anayenda limodzi msewu umodzi, ndipo mwadzidzidzi mngelo uja anachoka. 11 Koma Petulo atayamba kuzindikira zimene zikuchitika anati: “Tsopano ndadziwa kuti Yehova* ndi amene watumiza mngelo wake kudzandipulumutsa mʼmanja mwa Herode komanso ku zinthu zonse zimene Ayuda amayembekezera kuti zichitike.”+

12 Atazindikira zimenezi, iye anapita kunyumba kwa Mariya, mayi ake a Yohane wotchedwanso Maliko.+ Kumeneko anthu ambiri anali atasonkhana nʼkumapemphera. 13 Atagogoda pachitseko cha pageti mtsikana wantchito dzina lake Roda anapita kuti akaone amene akugogoda. 14 Koma atazindikira mawu a Petulo, anasangalala kwambiri moti mʼmalo motsegula getilo, anathamangira mkati nʼkukanena kuti Petulo ali pageti. 15 Koma iwo anamuyankha kuti: “Misalatu imeneyo!” Iye atalimbikira kuti akunena zoona, anthuwo anayamba kunena kuti: “Ndi mngelo wake ameneyo.” 16 Koma Petulo anapitiriza kugogoda. Iwo atatsegula, anaona kuti ndi iyeyodi ndipo anadabwa kwambiri. 17 Koma iye anawauza ndi manja kuti akhale chete, ndipo anawafotokozera mwatsatanetsatane mmene Yehova* anamutulutsira mʼndende. Kenako anati: “Nkhani imeneyi mukauze Yakobo+ ndi abale.” Atatero anatuluka nʼkupita kwina.

18 Kutacha, asilikali aja anasokonezeka kwambiri posadziwa zimene zachitikira Petulo. 19 Herode anafunafuna Petulo paliponse ndipo atalephera kumupeza, anapanikiza alonda aja ndi mafunso komanso analamula kuti awatenge nʼkukawapatsa chilango.+ Kenako Herode anachoka ku Yudeya nʼkupita ku Kaisareya, komwe anakhalako kwakanthawi ndithu.

20 Herode anakwiyira kwambiri* anthu a ku Turo ndi ku Sidoni. Choncho anthuwo anabwera kwa iye mogwirizana ndipo atamunyengerera Balasito, amene ankayangʼanira nyumba ya mfumu,* anapempha mtendere. Iwo anachita zimenezi chifukwa dziko lawo linkadalira chakudya chochokera mʼdziko la mfumuyo. 21 Pa tsiku lina lomwe anasankha, Herode anavala zovala zake zachifumu nʼkukhala pampando wake woweruzira milandu ndipo anayamba kulankhula ndi anthu. 22 Anthuwo atamva mawu ake anayamba kufuula kuti: “Amenewa ndi mawu a mulungu, osati a munthu!” 23 Nthawi yomweyo mngelo wa Yehova* anamudwalitsa, chifukwa sanalemekeze Mulungu. Ndipo anadyedwa ndi mphutsi nʼkufa.

24 Koma mawu a Yehova* anapitiriza kufalikira ndipo anthu ambiri anakhala okhulupirira.+

25 Baranaba+ ndi Saulo atamaliza ntchito yopereka thandizo ku Yerusalemu+ anabwerera. Popita anatenga Yohane,+ wotchedwanso Maliko.

13 Mumpingo wa ku Antiokeya munali aneneri ndi aphunzitsi.+ Iwo anali Baranaba, Sumiyoni wotchedwa Nigeri, Lukiyo wa ku Kurene, Saulo ndiponso Manayeni amene anaphunzira pamodzi ndi Herode wolamulira chigawo. 2 Pamene iwo ankatumikira Yehova* ndiponso kusala kudya, mzimu woyera unawauza kuti: “Mundipatulire Baranaba ndi Saulo+ kuti agwire ntchito imene ndinawaitanira.”+ 3 Atamaliza kusala kudya ndiponso kupemphera, anawagwira pamutu* nʼkuwalola kuti apite.

4 Choncho anthu amenewa, omwe anatumizidwa ndi mzimu woyera, anapita ku Selukeya ndipo kuchokera kumeneko anayenda ulendo wapamadzi kupita ku Kupuro. 5 Atafika mumzinda wa Salami anayamba kulalikira mawu a Mulungu mʼmasunagoge a Ayuda. Iwo analinso ndi Yohane yemwe ankawatumikira.*+

6 Iwo anayenda pachilumba chonse cha Kupuro mpaka kukafika ku Pafo. Kumeneko anakumana ndi Myuda wina wamatsenga dzina lake Bara-Yesu, yemwe analinso mneneri wabodza. 7 Iyeyu anali limodzi ndi bwanamkubwa Serigio Paulo, yemwe anali munthu wanzeru. Bwanamkubwayu anaitana Baranaba ndi Saulo, chifukwa ankafunitsitsa kumva mawu a Mulungu. 8 Koma Elima, wamatsenga, (chifukwa dzina lakeli amalimasulira chonchi) anayamba kutsutsana nawo. Iye ankayesetsa kuti bwanamkubwayo asakhulupirire Ambuye. 9 Koma Saulo, wotchedwanso Paulo, atadzazidwa ndi mzimu woyera, anamuyangʼanitsitsa 10 nʼkunena kuti: “Iwe munthu wodzaza ndi chinyengo chamtundu uliwonse ndiponso zoipa, mwana wa Mdyerekezi+ komanso mdani wa chinthu chilichonse cholungama, kodi udzasiya liti kupotoza njira zowongoka za Yehova?* 11 Tsopano tamvera! Dzanja la Yehova* lili pa iwe ndipo ukhala wakhungu. Kwakanthawi, suthanso kuona kuwala kwa dzuwa.” Nthawi yomweyo anaona nkhungu* yamphamvu mʼmaso mwake ndiponso mdima wandiweyani, ndipo anayamba kufufuza anthu oti amugwire dzanja ndi kumutsogolera. 12 Bwanamkubwa uja ataona zimenezi, anakhala wokhulupirira, chifukwa anadabwa kwambiri ndi zimene anaphunzira zokhudza Yehova.*

13 Kenako Paulo ndi anzakewo, anayamba ulendo wa panyanja kuchoka ku Pafo, ndipo anakafika ku Pega, ku Pamfuliya. Koma Yohane+ anawasiya nʼkubwerera ku Yerusalemu.+ 14 Atachoka ku Pega anakafika ku Antiokeya wa ku Pisidiya. Kumeneko analowa mʼsunagoge+ tsiku la Sabata nʼkukhala pansi. 15 Chilamulo ndi zimene aneneri analemba zitawerengedwa pamaso pa anthu,+ atsogoleri a sunagoge anatuma munthu kukawauza kuti: “Abale inu, ngati muli ndi mawu alionse amene angalimbikitse anthuwa, lankhulani.” 16 Choncho Paulo anaimirira ndipo anakweza dzanja lake nʼkunena kuti:

“Anthu inu, Aisiraeli, ndiponso ena nonsenu amene mumaopa Mulungu, tamverani. 17 Mulungu wa anthu awa Aisiraeli, anasankha makolo athu akale. Pamene iwo ankakhala mʼdziko lachilendo la Iguputo, iye anawasandutsa mtundu wamphamvu, ndipo anawatulutsa mʼdzikomo ndi dzanja lake lamphamvu.+ 18 Kwa zaka pafupifupi 40, iye anapirira khalidwe lawo mʼchipululu.+ 19 Ndipo atawononga mitundu 7 ya anthu mʼdziko la Kanani, anapereka dzikolo kwa Aisiraeli kuti likhale cholowa chawo.+ 20 Zonsezi zinachitika mʼzaka pafupifupi 450.

Zimenezi zitatha anawapatsa oweruza mpaka kudzafika pa nthawi ya mneneri Samueli.+ 21 Koma kenako anthuwo ananena kuti akufuna mfumu.+ Choncho Mulungu anawapatsa Sauli mwana wa Kisi, munthu wa fuko la Benjamini,+ ndipo anakhala mfumu yawo kwa zaka 40. 22 Atamuchotsa ameneyu, anawapatsa Davide kuti akhale mfumu yawo.+ Iyeyu Mulungu anamuchitira umboni kuti, ‘Ndapeza Davide mwana wa Jese,+ munthu wapamtima panga.+ Ameneyu adzachita zonse zimene ndikufuna.’ 23 Mogwirizana ndi lonjezo lake, kuchokera pa mbadwa* za munthu ameneyu, Mulungu wabweretsa mpulumutsi mu Isiraeli, amene ndi Yesu.+ 24 Mpulumutsi ameneyu asanafike, Yohane analalikira kwa anthu onse a ku Isiraeli za ubatizo, ngati chizindikiro cha kulapa.+ 25 Koma pamene Yohane ankamaliza utumiki wake, ankanena kuti, ‘Kodi mukuganiza kuti ndine ndani? Amene mukumuganizirayo si ine ayi. Koma wina akubwera pambuyo panga, amene ine si woyenera kumasula nsapato zake.’+

26 Anthu inu, abale anga, inu mbadwa za Abulahamu, ndi anthu onse oopa Mulungu amene muli nawo pamodziwa, mawu a chipulumutso chimenechi atumizidwa kwa ife.+ 27 Chifukwa anthu a ku Yerusalemu ndi olamulira awo sanamuzindikire. Koma pamene ankamuweruza, anakwaniritsa zimene aneneri ananena,+ zomwe zimawerengedwa mokweza sabata lililonse. 28 Ngakhale kuti sanapeze chifukwa chomuphera,+ anaumiriza Pilato kuti ameneyu aphedwe.+ 29 Ndiyeno atakwaniritsa zinthu zonse zimene zinalembedwa zokhudza iyeyo, anamutsitsa pamtengo nʼkumuika mʼmanda.*+ 30 Koma Mulungu anamuukitsa.+ 31 Ndipo kwa masiku ambiri anaonekera kwa anthu amene anayenda naye kuchokera ku Galileya kupita ku Yerusalemu. Panopa amenewa ndi mboni zake kwa anthu.+

32 Choncho ife tikulengeza kwa inu uthenga wabwino wonena za zinthu zimene makolo athu analonjezedwa. 33 Uthengawo ndi wakuti Mulungu wakwaniritsa zonse zimene anawalonjezazo kwa ife ana awo poukitsa Yesu,+ mogwirizana ndi zimene zinalembedwa mu salimo lachiwiri kuti: ‘Iwe ndiwe mwana wanga. Lero ine ndakhala bambo ako.’+ 34 Ndipo mfundo yakuti iye anamuukitsa ndipo sangabwererenso kuthupi limene limavunda,* anaifotokoza chonchi: ‘Ine ndidzakusonyezani anthu inu chikondi chokhulupirika chimene ndinalonjeza Davide. Lonjezo limeneli ndi lodalirika.’+ 35 Ndipo salimo lina limanenanso kuti, ‘Simudzalola kuti thupi la wokhulupirika wanu livunde.’+ 36 Davide anachita chifuniro cha Mulungu pa nthawi ya mʼbadwo wake, anamwalira nʼkuikidwa mʼmanda a makolo ake ndipo thupi lake linavunda.+ 37 Koma amene Mulungu anamuukitsa uja thupi lake silinavunde.+

38 Tsopano dziwani abale anga kuti, ife tikulalikira kwa inu za kukhululukidwa kwa machimo kudzera mwa ameneyu.+ 39 Dziwaninso kuti pa zinthu zonse zimene kunali kosatheka kuti muonedwe opanda mlandu kudzera mʼChilamulo cha Mose,+ aliyense wokhulupirira akuonedwa wopanda mlandu kudzera mwa iyeyu.+ 40 Choncho samalani kuti zimene aneneri analemba zisakugwereni, zomwe zimati: 41 ‘Inu onyoza onani zimene ine ndikuchita nʼkudabwa nazo. Kenako mudzatha, chifukwa simudzakhulupirira ngakhale pangʼono zimene ndidzachite mʼmasiku anu, ngakhale wina atakufotokozerani mwatsatanetsatane.’”+

42 Tsopano pamene ankatuluka, anthu anawachonderera kuti adzawafotokozerenso nkhani zimenezi Sabata lotsatira. 43 Choncho msonkhano wamʼsunagoge utatha, Ayuda ndi anthu ambiri omwe analowa Chiyuda amene ankalambira Mulungu anatsatira Paulo ndi Baranaba. Ndipo iwo anauza anthuwo kuti apitirize kukhala oyenera kulandira kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu.+

44 Sabata lotsatira, pafupifupi mzinda wonse unasonkhana kudzamvetsera mawu a Yehova.* 45 Ayuda ataona gulu la anthulo, anachita nsanje ndipo anayamba kutsutsa mwamwano zimene Paulo ankalankhula.+ 46 Choncho Paulo ndi Baranaba analankhula molimba mtima kuti: “Inu munali oyenera kuti muyambe kuuzidwa mawu a Mulungu.+ Koma popeza mukuwakana ndipo mukudziweruza nokha kuti ndinu osayenera moyo wosatha, ife tikupita kwa anthu a mitundu ina.+ 47 Ndipotu Yehova* watilamula kuti, ‘Ndakupatsani udindo woti mukhale kuwala kwa anthu a mitundu ina, kuti mukhale chipulumutso mpaka kumalekezero a dziko lapansi.’”+

48 Anthu a mitundu inawo atamva zimenezi, anasangalala ndipo anatamanda mawu a Yehova.* Anthu onse amene anali ndi maganizo abwino amene akanawathandiza kukapeza moyo wosatha anakhala okhulupirira. 49 Komanso, mawu a Yehova* anapitiriza kufalitsidwa mʼdziko lonselo. 50 Koma Ayuda anauza zoipa amayi otchuka oopa Mulungu komanso amuna olemekezeka amumzindawo. Choncho iwo anachititsa kuti Paulo ndi Baranaba ayambe kuzunzidwa+ ndipo anawaponya kunja kwa mzinda wawo. 51 Koma Paulo ndi Baranaba anasansa fumbi kumapazi awo kuti ukhale umboni wowatsutsa nʼkupita ku Ikoniyo.+ 52 Ndipo ophunzirawo anapitiriza kukhala osangalala+ komanso mzimu woyera unkawathandiza kwambiri.

14 Paulo ndi Baranaba ali ku Ikoniyo, analowa mʼsunagoge wa Ayuda ndipo analankhula bwino kwambiri moti Ayuda ambiri limodzi ndi Agiriki anakhala okhulupirira. 2 Koma Ayuda amene sanakhulupirire, anauza zoipa anthu a mitundu ina nʼkuwasokoneza maganizo kuti atsutsane ndi abalewo.+ 3 Choncho kwa nthawi yaitali, ankalankhula molimba mtima chifukwa cha mphamvu ya Yehova.* Iye anatsimikizira mawu a kukoma mtima kwake kwakukulu, polola kuti ophunzirawo azichita zizindikiro ndi zodabwitsa.+ 4 Koma gulu la anthu mumzindawo linagawanika. Ena anali kumbali ya Ayuda, ena kumbali ya atumwi. 5 Ndiyeno anthu a mitundu ina komanso Ayuda pamodzi ndi olamulira awo, anakonza chiwembu kuti achitire chipongwe atumwiwo nʼkuwaponya miyala.+ 6 Koma iwo atadziwitsidwa zimenezi, anathawira mʼmizinda ya Lukaoniya, Lusitara, Debe, ndi mʼmadera ozungulira.+ 7 Kumeneko anapitiriza kulalikira uthenga wabwino.

8 Ku Lusitara, kunali munthu wina wolumala miyendo ndipo anali atakhala pansi. Iyeyu anabadwa wolumala ndipo anali asanayendepo. 9 Munthu ameneyu ankamvetsera pamene Paulo ankalankhula. Ndiyeno Paulo atamuyangʼanitsitsa anaona kuti ali ndi chikhulupiriro choti angachiritsidwe.+ 10 Choncho Paulo analankhula mokweza mawu kuti: “Imirira!” Atatero, wolumalayo anadumpha nʼkuyamba kuyenda.+ 11 Gulu la anthu litaona zimene Paulo anachitazo, linafuula mʼchilankhulo cha Chilukaoniya kuti: “Milungu yakhala ngati anthu ndipo yatsikira kwa ife!”+ 12 Choncho Baranaba anayamba kumutchula kuti Zeu, koma Paulo ankamutchula kuti Heme, chifukwa ndi amene ankatsogolera polankhula. 13 Ndiyeno wansembe wa Zeu, amene kachisi wake anali pafupi ndi polowera mumzindawo, anabweretsa ngʼombe zamphongo ndi nkhata zamaluwa pamageti. Iye ankafuna kupereka nsembe pamodzi ndi gulu la anthulo.

14 Koma atumwiwo, Baranaba ndi Paulo, atamva zimenezi anangʼamba malaya awo akunja nʼkuthamanga kukalowa mʼgulu la anthu lija akufuula kuti: 15 “Anthu inu, mukuchitiranji zimenezi? Ifenso ndife anthu okhala ndi zofooka ngati inu nomwe.+ Tikulengeza uthenga wabwino kwa inu kuti musiye zinthu zachabechabezi nʼkuyamba kulambira Mulungu wamoyo, amene anapanga kumwamba, dziko lapansi, nyanja ndi zonse zokhala mmenemo.+ 16 Mʼmibadwo yamʼmbuyomu iye analola anthu a mitundu yonse kuti aziyenda mʼnjira zawo.+ 17 Komabe iye sanangokhala wopanda umboni+ wakuti anachita zabwino. Anakupatsani mvula kuchokera kumwamba ndi nyengo zimene zokolola zanu zimakhala zambiri.+ Anadzaza mitima yanu ndi chakudya komanso chisangalalo.”+ 18 Ngakhale kuti atumwiwo ananena zimenezi, anavutikabe kuletsa gulu la anthulo kupereka nsembe kwa iwo.

19 Ndiyeno Ayuda amene anabwera kuchokera ku Antiokeya ndi ku Ikoniyo anakopa anthuwo.+ Choncho anaponya Paulo miyala nʼkumukokera kunja kwa mzindawo poganiza kuti wafa.+ 20 Koma pamene ophunzira anamuzungulira, anadzuka nʼkukalowa mumzinda. Tsiku lotsatira iye pamodzi ndi Baranaba anachoka nʼkupita ku Debe.+ 21 Atalengeza uthenga wabwino mumzindawu nʼkuphunzitsa anthu ambiri ndithu kuti akhale ophunzira, anabwerera ku Lusitara, ku Ikoniyo ndi ku Antiokeya. 22 Mʼmalo onsewa ankalimbitsa ophunzira+ komanso kuwathandiza kuti apitirize kukhala ndi chikhulupiriro. Ankawauza kuti: “Tiyenera kukumana ndi mavuto ambiri kuti tikalowe mu Ufumu wa Mulungu.”+ 23 Anasankhanso akulu mumpingo uliwonse,+ ndipo atapemphera komanso kusala kudya,+ anawapereka kwa Yehova* yemwe anamukhulupirira.

24 Kenako anadutsa ku Pisidiya nʼkupita ku Pamfuliya.+ 25 Atamaliza kulalikira mawu a Mulungu ku Pega, anapita ku Ataliya. 26 Pochoka kumeneko anayenda ulendo wapamadzi kubwerera ku Antiokeya. Kumeneku nʼkumene mʼmbuyomo abale anawasankha kuti Mulungu awasonyeze kukoma mtima kwakukulu nʼcholinga choti agwire ntchito, yomwe tsopano pa nthawiyi anali ataimaliza.+

27 Atafika kumeneko anasonkhanitsa anthu amumpingo ndipo anawafotokozera zinthu zambiri zimene Mulungu anachita kudzera mwa iwo. Anawafotokozeranso kuti Mulungu anatsegulanso khomo kuti anthu a mitundu ina akhale okhulupirira.+ 28 Choncho anakhala ndi ophunzirawo kwa kanthawi ndithu.

15 Ndiyeno amuna ena ochokera ku Yudeya anayamba kuphunzitsa abale kuti: “Mukapanda kudulidwa mogwirizana ndi mwambo wa Mose,+ simungapulumuke.” 2 Koma Paulo ndi Baranaba sanagwirizane nazo ndipo anatsutsana nawo. Choncho iwo anasankha Paulo, Baranaba komanso anthu ena, kuti apite kwa atumwi ndi akulu ku Yerusalemu+ kukawauza za nkhaniyi.

3 Mpingo utawaperekeza, anthu amenewa anapitiriza ulendo wawo kudzera ku Foinike ndi ku Samariya. Kumeneko ankafotokoza mwatsatanetsatane zoti anthu a mitundu ina ayamba kulambira Mulungu, ndipo abale onse anasangalala kwambiri ndi zimenezi. 4 Atafika ku Yerusalemu analandiridwa ndi manja awiri ndi mpingo, atumwi komanso akulu. Ndipo anafotokoza zinthu zambiri zimene Mulungu anachita kudzera mwa iwowo. 5 Koma okhulupirira ena, amene kale anali mʼgulu lampatuko la Afarisi, anaimirira mʼmipando yawo nʼkunena kuti: “Mʼpofunika kuwadula komanso kuwalamula kuti azisunga Chilamulo cha Mose.”+

6 Choncho atumwi ndi akulu anasonkhana kuti akambirane za nkhani imeneyi. 7 Atatsutsana kwambiri za nkhaniyi, Petulo anaimirira nʼkuwauza kuti: “Abale anga, mukudziwa bwino kuti mʼmasiku oyambirira Mulungu anandisankha ine pakati panu, kuti kudzera pakamwa panga, anthu a mitundu ina amve mawu a uthenga wabwino nʼkukhulupirira.+ 8 Ndipo Mulungu, amene amadziwa zamumtima,+ anachitira umboni powapatsa mzimu woyera+ ngati mmene anachitiranso kwa ife. 9 Iye sanasiyanitse mʼpangʼono pomwe pakati pa ife ndi iwo.+ Koma anayeretsa mitima yawo chifukwa cha chikhulupiriro chawo.+ 10 Ndiye nʼchifukwa chiyani inu mukumuyesa Mulungu posenzetsa ophunzira goli+ limene makolo athu ngakhalenso ifeyo sitinathe kulisenza?+ 11 Koma tsopano tikukhulupirira kuti ife tidzapulumuka chifukwa cha kukoma mtima kwakukulu kwa Ambuye Yesu,+ mofanananso ndi anthu amenewa.”+

12 Zitatero gulu lonselo linakhala chete, ndipo linayamba kumvetsera pamene Baranaba ndi Paulo ankafotokoza zizindikiro ndi zodabwitsa zambiri zimene Mulungu anachita pakati pa anthu a mitundu ina kudzera mwa iwo. 13 Atamaliza kulankhula, Yakobo anayankha kuti: “Abale anga, ndimvetsereni. 14 Sumiyoni+ wafotokoza bwino mmene Mulungu anacheukira anthu a mitundu ina kwa nthawi yoyamba, kuti pakati pawo atengepo anthu odziwika ndi dzina lake.+ 15 Ndipo zimenezi zikugwirizana ndi zimene aneneri analemba zakuti: 16 ‘Zimenezi zikadzatha ndidzabwerera nʼkumanganso tenti* ya Davide imene inagwa. Ndidzamanganso malo ogumuka a nyumbayo nʼkuikonzanso. 17 Ndidzachita zimenezi kuti anthu otsalawo afunefune Yehova* ndi mtima wonse. Amufunefune pamodzi ndi mitundu yonse ya anthu, anthu otchedwa ndi dzina langa, watero Yehova* amene akuchita zinthu zimenezi,+ 18 zomwe anatsimikiza kalekale kuti adzazichita.’+ 19 Choncho chigamulo* changa nʼchakuti, anthu a mitundu ina amene ayamba kulambira Mulungu, tisawavutitse.+ 20 Koma tiyeni tiwalembere kuti apewe zinthu zoipitsidwa ndi mafano,+ chiwerewere,*+ zopotola* ndi magazi.+ 21 Chifukwa kuyambira kalekale, anthu akhala akulalikira mumzinda ndi mzinda mawu ochokera mʼmabuku a Mose, popeza mabuku amenewa amawerengedwa mokweza mʼmasunagoge sabata lililonse.”+

22 Kenako atumwi ndi akulu pamodzi ndi mpingo wonse, anagwirizana zosankha amuna pakati pawo, kuti awatumize ku Antiokeya limodzi ndi Paulo ndi Baranaba. Choncho anasankha Yudasi wotchedwa Barasaba ndi Sila,+ omwe ankatsogolera abale. 23 Ndiyeno analemba kalata nʼkuwapatsira yonena kuti:

“Ife abale anu atumwi pamodzi ndi akulu, tikulembera inu abale athu ochokera mʼmitundu ina, amene muli ku Antiokeya,+ ku Siriya ndi ku Kilikiya: Landirani moni! 24 Tamva kuti ena ochokera pakati pathu akhala akukuvutitsani polankhula zinthu zokusokonezani,+ ngakhale kuti ife sitinawapatse malangizo aliwonse. 25 Choncho tonse tagwirizana kuti tisankhe amuna nʼkuwatumiza pamodzi ndi abale athu okondedwa, Baranaba ndi Paulo. 26 Anthu amenewa apereka miyoyo yawo chifukwa cha dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu.+ 27 Tikutumiza Yudasi ndi Sila, kuti iwonso adzakufotokozereni zinthu zomwezi ndi mawu apakamwa.+ 28 Chifukwa mzimu woyera+ komanso ifeyo taona kuti ndi bwino kuti tisakusenzetseni mtolo wolemera, kupatula zinthu zofunika zokhazi zomwe ndi 29 kupitiriza kupewa zinthu zoperekedwa nsembe kwa mafano,+ magazi,+ zopotola*+ ndi chiwerewere.*+ Mukamapewa zinthu zimenezi mosamala kwambiri, zinthu zidzakuyenderani bwino. Tikukufunirani zabwino zonse!”*

30 Amuna amenewa atanyamuka, anapita ku Antiokeya. Kumeneko anasonkhanitsa gulu lonse la anthu nʼkuwapatsa kalatayo. 31 Ataiwerenga, anasangalala chifukwa cha mawu olimbikitsawo. 32 Popeza Yudasi ndi Sila analinso aneneri, anawakambira abalewo nkhani zambiri ndipo anawalimbikitsa.+ 33 Atakhala kumeneko kwakanthawi, abalewo anawaperekeza ndipo anabwerera mwamtendere kwa amene anawatuma. 34* ⁠—— 35 Koma Paulo ndi Baranaba anatsala ku Antiokeya. Iwo pamodzi ndi anthu enanso ambiri ankaphunzitsa komanso kulengeza uthenga wabwino wa mawu a Yehova.*

36 Patapita masiku, Paulo anauza Baranaba kuti: “Tiyeni tibwerere kumizinda yonse kumene tinalalikira mawu a Yehova* kuti tikachezere abale ndiponso tikawaone kuti ali bwanji.”+ 37 Baranaba ankafunitsitsa kuti atenge Yohane, wotchedwanso Maliko.+ 38 Koma Paulo anaona kuti si bwino kumutenga chifukwa ulendo wina Yohane anawasiya ku Pamfuliya ndipo sanapite nawo ku ntchitoyi.+ 39 Zitatero anakangana koopsa mpaka anasiyana. Baranaba+ anatenga Maliko ndipo anayenda ulendo wapamadzi kupita ku Kupuro. 40 Koma Paulo anasankha Sila, ndipo abale atamupempherera Pauloyo kuti Yehova* amusonyeze kukoma mtima kwakukulu, ananyamuka.+ 41 Iye anadzera ku Siriya ndi ku Kilikiya ndipo ankalimbikitsa mipingo.

16 Kenako Paulo anafika ku Debe ndiponso ku Lusitara.+ Kumeneko kunali wophunzira wina dzina lake Timoteyo,+ mwana wa mayi wa Chiyuda wokhulupirira, koma bambo ake anali Mgiriki. 2 Abale a ku Lusitara ndi ku Ikoniyo anapereka umboni wabwino wonena za iyeyo. 3 Paulo anasonyeza kuti akufuna kumutenga pa ulendo wake. Choncho anamutenga nʼkumudula chifukwa cha Ayuda amene anali kumeneko,+ popeza onse ankadziwa kuti bambo ake ndi Mgiriki. 4 Mʼmizinda yonse imene ankadutsa, ankapatsa okhulupirira akumeneko malamulo oyenera kuwatsatira, mogwirizana ndi zimene atumwi ndiponso akulu ku Yerusalemu anagamula.+ 5 Choncho anthu mʼmipingo anapitiriza kukhala ndi chikhulupiriro cholimba ndipo chiwerengero chinkawonjezeka tsiku ndi tsiku.

6 Kenako iwo anapita ku Fulugiya ndiponso mʼdziko la Galatiya,+ chifukwa mzimu woyera unawaletsa kulankhula mawu a Mulungu mʼchigawo cha Asia. 7 Atafika ku Musiya anayesetsa kuti apite ku Bituniya,+ koma mzimu wa Yesu sunawalole. 8 Choncho anangodutsa ku Musiya nʼkukafika ku Torowa. 9 Ndiyeno usiku Paulo anaona masomphenya. Anaona munthu wina wa ku Makedoniya ataima nʼkumuuza kuti: “Wolokerani ku Makedoniya kuno mudzatithandize.” 10 Atangoona masomphenya amenewo, tinaganiza zopita ku Makedoniya. Tinatsimikiza kuti Mulungu watiitana kuti tikalengeze uthenga wabwino kwa anthu akumeneko.

11 Choncho tinanyamuka ulendo wapanyanja kuchokera ku Torowa kupita ku Samatirake. Koma tsiku lotsatira tinafika ku Neapoli. 12 Titachoka kumeneko tinafika ku Filipi,+ mzinda wolamulidwa ndi Aroma, umenenso ndi likulu la chigawo cha Makedoniya. Tinakhala mumzindawu kwa masiku angapo. 13 Tsiku la sabata tinatuluka pageti nʼkupita mʼmbali mwa mtsinje, kumene tinkaganiza kuti kuli malo opempherera. Kenako tinakhala pansi nʼkuyamba kulankhula ndi azimayi amene anasonkhana kumeneko. 14 Pagululo panali mayi wina dzina lake Lidiya ndipo anali wolambira Mulungu. Iye ankachokera mumzinda wa Tiyatira+ ndipo ankagulitsa nsalu ndi zovala zapepo. Pamene ankamvetsera, Yehova* anatsegula kwambiri mtima wake kuti amvetse zimene Paulo ankalankhula. 15 Iye ndi anthu a mʼbanja lake atabatizidwa+ anatipempha kuti: “Abale anga, ngati mwaona kuti ndine wokhulupirika kwa Yehova,* tiyeni mukakhale kwathu.” Moti anatitenga kuti tipite kwawo.

16 Ndiyeno pamene tinkapita kumalo opempherera, tinakumana ndi mtsikana wina wantchito wogwidwa ndi mzimu, chiwanda cholosera zamʼtsogolo.+ Iye ankachititsa kuti mabwana ake azipindula kwambiri chifukwa cha zoloserazo. 17 Mtsikana ameneyu ankangotsatira Paulo ndi ifeyo nʼkumafuula kuti: “Anthu awa ndi akapolo a Mulungu Wamʼmwambamwamba+ ndipo akulengeza njira ya chipulumutso kwa inu.” 18 Iye anachita zimenezi kwa masiku ambiri. Kenako Paulo anatopa nazo ndipo anatembenuka nʼkuuza mzimuwo kuti: “Ndikukulamula mʼdzina la Yesu Khristu kuti utuluke mwa mtsikanayu.” Nthawi yomweyo mzimuwo unatuluka.+

19 Koma mabwana ake aja ataona kuti sapindulanso,+ anagwira Paulo ndi Sila nʼkuwakokera mumsika, kubwalo la olamulira.+ 20 Atafika nawo kwa akuluakulu a zamalamulo, ananena kuti: “Anthu awa akusokoneza kwambiri mzinda wathu,+ komanso iwowa ndi Ayuda. 21 Ndipo akufalitsa miyambo imene kwa ife ndi yosaloleka kuitsatira kapena kuichita, popeza ndife Aroma.” 22 Kenako gulu lonselo linanyamuka nʼkuukira atumwiwo. Ndipo akuluakulu a zamalamulowo, anavula atumwiwo malaya awo mochita kuwangʼambira nʼkulamula kuti awakwapule ndi ndodo.+ 23 Atawakwapula zikoti zambiri, anawatsekera mʼndende ndi kulamula woyangʼanira ndende kuti aziwalondera nʼcholinga choti asathawe.+ 24 Popeza kuti anamulamula zimenezi, iye anakawaika mʼchipinda chamkati cha ndendeyo nʼkumanga mapazi awo mʼmatangadza.

25 Koma chapakati pa usiku, Paulo ndi Sila anayamba kupemphera ndiponso kutamanda Mulungu poimba nyimbo,+ moti akaidi ena ankawamva. 26 Mwadzidzidzi panachitika chivomerezi champhamvu, mpaka maziko a ndendeyo anagwedezeka. Nthawi yomweyo zitseko zonse zinatseguka, ndipo aliyense unyolo wake unamasuka.+ 27 Woyangʼanira ndende uja atadzuka nʼkuona kuti zitseko za ndende nʼzotseguka, anasolola lupanga lake kuti adziphe, poganiza kuti akaidiwo athawa.+ 28 Koma Paulo anafuula kuti: “Usadzivulaze, tonse tilipo!” 29 Iye anapempha kuti amupatse nyale ndipo mwamsanga analowa mkatimo. Akunjenjemera ndi mantha, anagwada patsogolo pa Paulo ndi Sila. 30 Kenako anawatulutsa kunja nʼkunena kuti: “Mabwana, ndichite chiyani kuti ndipulumuke?” 31 Iwo anati: “Khulupirira Ambuye Yesu ndipo udzapulumuka limodzi ndi anthu a mʼnyumba yako.”+ 32 Kenako analankhula mawu a Yehova* kwa iye pamodzi ndi onse a mʼnyumba yake. 33 Usiku womwewo, anawatenga nʼkuwatsuka mabala awo. Pasanapite nthawi yaitali, iye ndi anthu onse a mʼbanja lake anabatizidwa.+ 34 Kenako anapita nawo kunyumba kwake nʼkuwaikira chakudya patebulo. Ndipo iye limodzi ndi onse a mʼbanja lake, anasangalala kwambiri chifukwa anakhulupirira Mulungu.

35 Mʼmawa mwake, akuluakulu a zamalamulo anatumiza asilikali kukanena kuti: “Anthu amenewo amasuleni.” 36 Choncho woyangʼanira ndende uja anauza Paulo uthengawo kuti: “Akuluakulu a zamalamulo atumiza anthu kudzanena kuti awirinu mumasulidwe. Choncho tulukani tsopano, ndipo mupite mwamtendere.” 37 Koma Paulo anawauza kuti: “Iwo atikwapula pamaso pa anthu nʼkutitsekera mʼndende popanda kutizenga mlandu, chikhalirecho ndife Aroma.+ Kodi tsopano akutitulutsa mwamseri? Ayi, zimenezo sizitheka! Abwere eniakewo adzatitulutse okha.” 38 Ndiyeno asilikaliwo anakanena zimenezi kwa akuluakulu a zamalamulo aja. Akuluakulu a zamalamulowo anachita mantha atamva kuti anthuwo ndi Aroma.+ 39 Choncho iwo anabwera nʼkuwachonderera, ndipo atawatulutsa anawapempha kuti achoke mumzindawo. 40 Koma iwo atatuluka mʼndendemo anapita kunyumba kwa Lidiya. Ataona abale anawalimbikitsa,+ kenako ananyamuka nʼkumapita.

17 Kenako iwo anayenda kudutsa ku Amfipoli ndi ku Apoloniya ndipo anafika ku Tesalonika,+ kumene kunali sunagoge wa Ayuda. 2 Choncho mwachizolowezi chake,+ Paulo analowa mʼsunagogemo ndipo kwa milungu itatu anakambirana nawo mfundo za mʼMalemba.+ 3 Iye ankafotokoza ndiponso kusonyeza umboni wolembedwa powatsimikizira kuti zinali zoyenera kuti Khristu avutike,+ kenako auke.+ Ankanena kuti: “Yesu amene ndikumulalikira kwa inu, ndiye Khristu.” 4 Pamapeto pake, ena mwa iwo anakhala okhulupirira ndipo anagwirizana ndi Paulo ndi Sila.+ Agiriki ambiri opembedza Mulungu komanso azimayi ambiri olemekezeka anachitanso chimodzimodzi.

5 Koma Ayuda anachita nsanje+ ndipo anasonkhanitsa anthu ena oipa amene ankangokhala pamsika. Iwowa anapanga gulu lachiwawa nʼkuyambitsa chipolowe mumzindamo. Kenako anapita kunyumba ya Yasoni, kukafuna Paulo ndi Sila kuti awatulutse nʼkuwapereka ku gulu limene linkachita chipolowelo. 6 Atalephera kuwapeza, anakokera Yasoni ndi abale ena kwa olamulira a mzindawo, akufuula kuti: “Anthu awa, amene ayambitsa mavuto kwina konseku, tsopano akupezekanso kuno.+ 7 Ndipo Yasoni wawalandira ngati alendo ake. Anthu onsewa akuchita zotsutsana ndi malamulo a Kaisara. Eti akunena kuti kulinso mfumu ina dzina lake Yesu.”+ 8 Atanena mawu amenewa, gulu la anthu lija komanso olamulira a mzindawo anakwiya kwambiri. 9 Olamulira a mzindawo analipiritsa Yasoni ndi enawo ndalama,* kenako anawamasula.

10 Kutangoda, abale anatulutsa Paulo ndi Sila nʼkuwatumiza ku Bereya. Iwo atafika kumeneko, analowa mʼsunagoge wa Ayuda. 11 Koma anthu a ku Bereya anali a mtima wofuna kuphunzira kuposa a ku Tesalonika aja. Iwowa analandira mawu a Mulungu ndi chidwi chachikulu kwambiri, ndipo tsiku ndi tsiku ankafufuza Malemba mosamala kuti atsimikizire ngati zimene anamvazo zinalidi zoona. 12 Ambiri mwa anthu amenewa anakhala okhulupirira, chimodzimodzinso akazi ndi amuna ena otchuka a Chigiriki. 13 Koma Ayuda ochokera ku Tesalonika atamva kuti Paulo akufalitsanso mawu a Mulungu ku Bereya, anapitanso kumeneko kukachititsa anthu kuti akwiyire atumwiwo nʼkuyambitsa chipolowe.+ 14 Nthawi yomweyo abale anatumiza Paulo kuti apite kunyanja.+ Koma Sila ndi Timoteyo anatsala komweko. 15 Ndipo anthu amene anaperekeza Paulo anakamufikitsa ku Atene. Koma anabwerera atatumidwa kuti akauze Sila ndi Timoteyo+ kuti atsatire Pauloyo mwamsanga.

16 Pamene Paulo ankawayembekezera ku Atene, mtima unamuwawa kwambiri poona kuti mumzindawo mwadzaza mafano. 17 Atalowa mʼsunagoge anayamba kukambirana ndi Ayuda ndi anthu ena opembedza Mulungu. Ndipo tsiku ndi tsiku ankakambirananso ndi anthu amene ankawapeza pamsika. 18 Koma anthu ena anzeru za Epikureya ndi Sitoiki anayamba kutsutsana naye. Ena ankanena kuti: “Kodi nayenso wobwetuka uyu akufuna kunena chiyani?” Pomwe ena ankanena kuti: “Akuoneka kuti akulalikira za milungu yachilendo.” Ankanena zimenezi chifukwa chakuti Paulo ankalengeza uthenga wabwino wa Yesu ndi za kuuka kwa akufa.+ 19 Choncho anamugwira nʼkupita naye kubwalo la Areopagi nʼkumuuza kuti: “Kodi tingadziweko za chiphunzitso chatsopano chimene ukuphunzitsachi? 20 Chifukwatu zimene ukufotokozazi ndi zinthu zachilendo mʼmakutu mwathu. Ndiye tikufuna tidziwe tanthauzo lake.” 21 Ndipotu anthu onse a ku Atene ndi alendo ogonera kumeneko, ankathera nthawi yawo yonse yopuma akufotokoza kapena kumvetsera nkhani zatsopano. 22 Tsopano Paulo anaima pakati pa bwalo la Areopagi+ nʼkunena kuti:

“Inu anthu a ku Atene, ndaona kuti pa zinthu zonse mumaopa kwambiri milungu* kuposa mmene ena amachitira.+ 23 Mwachitsanzo, pamene ndimadutsa nʼkumayangʼanitsitsa zinthu zimene mumalambira, ndapezanso guwa lansembe lolembedwa kuti, ‘Kwa Mulungu Wosadziwika.’ Choncho ine ndikulalikira kwa inu za Mulungu wosadziwika amene mukumulambirayo. 24 Mulungu amene anapanga dzikoli ndi zinthu zonse zili mmenemu, sakhala mu akachisi opangidwa ndi manja.+ Iye ndiye Ambuye wakumwamba ndi dziko lapansi.+ 25 Komanso satumikiridwa ndi manja a anthu ngati kuti amasowa kanthu,+ chifukwa ndi iyeyo amene amapatsa anthu onse moyo, mpweya+ ndi zinthu zonse. 26 Ndipo kuchokera mwa munthu mmodzi+ anapanga mitundu yonse ya anthu, kuti akhale padziko lonse lapansi.+ Iye anaika nthawi yoti zinthu zina zizichitika komanso anaika malire a malo oti anthu azikhala.+ 27 Anachita zimenezi kuti anthuwo afunefune Mulungu, amufufuzefufuze nʼkumupezadi,+ ngakhale kuti kwenikweni, iye sali kutali ndi aliyense wa ife. 28 Paja chifukwa cha iye tili ndi moyo, timayenda ndipo tilipo, ngati mmene andakatulo anu ena ananenera kuti, ‘Paja ndife ana ake.’*

29 Choncho, popeza ndife ana a Mulungu,+ tisaganize kuti Mulunguyo ali ngati golide, siliva, mwala kapena chilichonse chosemedwa ndi anthu aluso.+ 30 Nʼzoona kuti Mulungu analekerera nthawi yomwe anthu sankadziwa zinthu,+ koma tsopano akuuza anthu kwina kulikonse kuti onse alape. 31 Chifukwa wakhazikitsa tsiku limene akufuna kudzaweruza+ mwachilungamo dziko lonse lapansi, kudzera mwa munthu amene iye wamusankha. Ndipo watsimikizira anthu onse zimenezi pomuukitsa.”+

32 Ndiyeno anthuwo atamva za kuuka kwa akufa, ena anayamba kuseka mwachipongwe,+ pomwe ena anati: “Chabwino, udzatiuzenso zimenezi nthawi ina.” 33 Choncho Paulo anawasiya. 34 Koma anthu ena anakhala kumbali yake ndipo anakhala otsatira a Yesu. Ena mwa iwo anali Diyonisiyo, woweruza mʼbwalo la Areopagi, mayi wina dzina lake Damarisi komanso anthu ena.

18 Kenako Paulo anachoka ku Atene nʼkupita ku Korinto. 2 Kumeneko anapeza Myuda wina dzina lake Akula,+ wa ku Ponto. Iyeyu pamodzi ndi mkazi wake Purisila, anali atangofika kumene kuchokera ku Italy, chifukwa Kalaudiyo anali atalamula Ayuda onse kuti achoke ku Roma. Choncho Paulo anapita kunyumba kwawo. 3 Popeza ntchito yawo inali imodzi, anakhala kunyumba kwawoko. Iwo ankagwirira ntchito limodzi,+ chifukwa onse anali opanga matenti. 4 Paulo ankakamba nkhani mʼsunagoge+ tsiku la sabata lililonse+ ndipo ankakopa Ayuda ndi Agiriki.

5 Sila+ ndi Timoteyo+ atafika kuchokera ku Makedoniya, Paulo anatanganidwa kwambiri ndi ntchito yolalikira mawu a Mulungu. Iye ankachitira umboni kwa Ayuda ndiponso kuwatsimikizira kuti Yesu ndiyedi Khristu.+ 6 Koma iwo atapitiriza kumutsutsa ndiponso kumunyoza, iye anakutumula zovala zake+ nʼkuwauza kuti: “Magazi anu akhale pamutu panu.+ Ine ndilibe mlandu.+ Kuyambira panopa ndizipita kwa anthu a mitundu ina.”+ 7 Zitatero, iye anachoka kumeneko* nʼkupita kunyumba ya munthu wina dzina lake Titiyo Yusito. Munthuyu anali wolambira Mulungu ndipo nyumba yake inali moyandikana ndi sunagoge. 8 Kirisipo,+ mtsogoleri wa sunagoge, anakhulupirira Ambuye pamodzi ndi anthu onse a mʼbanja lake. Ndipo anthu ambiri a ku Korinto, amene anamva uthenga wabwino, anayamba kukhulupirira nʼkubatizidwa. 9 Komanso usiku, Ambuye anauza Paulo mʼmasomphenya kuti: “Usaope, pitiriza kulankhula. Usakhale chete, 10 chifukwa ine ndili nawe.+ Palibe munthu amene adzakukhudze nʼkukuvulaza, popeza ndili ndi anthu ambiri mumzindawu.” 11 Choncho anakhala kumeneko chaka ndi miyezi 6, akuwaphunzitsa mawu a Mulungu.

12 Pamene Galiyo anali bwanamkubwa* wa Akaya, Ayuda ananyamuka mogwirizana nʼkuukira Paulo ndipo anamutengera kumpando woweruzira milandu. 13 Kumeneko iwo anati: “Munthu uyu akukopa anthu kuti azipembedza Mulungu mʼnjira yosemphana ndi chilamulo.” 14 Koma pamene Paulo ankati azitsegula pakamwa, Galiyo anauza Ayudawo kuti: “Ayuda inu, chikanakhala cholakwa china kapena mlandu waukulu, ndithu ndikanaleza mtima nʼkukumvetserani. 15 Koma ngati nkhani yake ili yokhudza mikangano pa mawu, mayina ndi chilamulo chanu,+ zimenezo muthane nazo nokha. Ine sindikufuna kuti ndikhale woweruza nkhani zoterezi.” 16 Atatero anawauza kuti achoke kumpando woweruzira milanduwo. 17 Zitatero, onse anagwira Sositene,+ mtsogoleri wa sunagoge nʼkuyamba kumumenya pafupi ndi mpando woweruzira milanduwo. Koma zimenezi sizinamukhudze Galiyo ngakhale pangʼono.

18 Paulo atakhala kumeneko kwa masiku ndithu, anatsanzikana ndi abalewo ndipo anapitiriza ulendo wake wapamadzi kulowera ku Siriya. Pa ulendowu anapita limodzi ndi Purisila ndi Akula. Paulo anameta tsitsi lake ku Kenkereya+ chifukwa cha lonjezo limene anachita. 19 Choncho onse anafika ku Efeso, ndipo anzakewo anawasiya kumeneko. Koma iye yekha analowa mʼsunagoge nʼkuyamba kukambirana ndi Ayuda.+ 20 Ngakhale kuti anamupempha mobwerezabwereza kuti akhale nawo kwa masiku ambiri, iye sanalole. 21 Mʼmalomwake, anatsanzikana nawo nʼkuwauza kuti: “Yehova* akalola ndidzabweranso kudzakuonani.” Choncho ananyamuka ku Efeso ulendo wapanyanja 22 ndipo anafika ku Kaisareya. Kenako anapita* kukapereka moni ku mpingo ndipo pambuyo pake anapita ku Antiokeya.+

23 Atakhala kumeneko kwa kanthawi, ananyamuka nʼkuyamba kuyenda malo osiyanasiyana mʼchigawo cha Galatiya ndi Fulugiya+ ndipo ankalimbikitsa ophunzira onse.+

24 Tsopano Myuda wina dzina lake Apolo,+ wa ku Alekizandiriya, amene ankalankhula mwaluso, anafika ku Efeso. Iyeyu ankadziwanso bwino Malemba. 25 Mwamuna ameneyu anaphunzitsidwa* njira ya Yehova.* Iye anali wodzipereka kwambiri chifukwa chakuti anali ndi mzimu woyera, ndipo ankalankhula ndi kuphunzitsa molondola za Yesu. Koma ankangodziwa za ubatizo wa Yohane wokha. 26 Munthu ameneyu anayamba kulankhula molimba mtima musunagoge. Ndiyeno Purisila ndi Akula+ atamumvetsera, anamutenga nʼkumufotokozera njira ya Mulungu molondola. 27 Ndiponso, popeza kuti ankafunitsitsa kupita ku Akaya, abalewo analembera ophunzira kumeneko. Anawalimbikitsa kuti amulandire ndi manja awiri. Choncho iye atafika kumeneko, anathandiza kwambiri anthu amene anali atakhulupirira chifukwa cha kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu. 28 Chifukwa iye anawatsimikizira Ayuda poyera komanso mwamphamvu kuti anali olakwa, ndipo anagwiritsa ntchito Malemba posonyeza kuti Yesu ndiyedi Khristu.+

19 Nthawi inayake, Apolo+ ali ku Korinto, Paulo anadzera kumadera akumtunda mpaka anafika ku Efeso.+ Kumeneko anapezako ophunzira ena, 2 ndipo anawafunsa kuti: “Kodi munalandira mzimu woyera mutakhala okhulupirira?”+ Iwo anamuyankha kuti: “Ifetu sitinamvepo kuti kuli mzimu woyera.” 3 Iye anawafunsanso kuti: “Nanga munabatizidwa ubatizo wamtundu wanji?” Iwo anayankha kuti: “Tinabatizidwa ubatizo wa Yohane.”+ 4 Kenako Paulo anati: “Ubatizo umene Yohane ankabatiza anthu unali chizindikiro chakuti munthu walapa.+ Ankauza anthu kuti akhulupirire amene akubwera mʼmbuyo mwake,+ kutanthauza Yesu.” 5 Atamva zimenezi, anthuwo anabatizidwa mʼdzina la Ambuye Yesu. 6 Ndiyeno Paulo atawagwira pamutu,* iwo analandira mzimu woyera+ ndipo anayamba kulankhula malilime* komanso kunenera.+ 7 Onse pamodzi anali amuna pafupifupi 12.

8 Kwa miyezi itatu, Paulo ankapita kusunagoge+ kumene ankalankhula molimba mtima. Kumeneko ankakamba nkhani ndiponso kuwafotokozera mfundo zogwira mtima zokhudza Ufumu wa Mulungu.+ 9 Koma ena anapitiriza kuchita makani komanso sankakhulupirira, ndipo ankanena zonyoza Njirayo+ pamaso pa anthu ambiri. Choncho iye anawachokera+ nʼkuchotsanso ophunzirawo pakati pawo. Ndipo tsiku ndi tsiku ankakamba nkhani muholo pasukulu ya Turano. 10 Izi zinachitika kwa zaka ziwiri, moti anthu onse okhala mʼchigawo cha Asia, Ayuda ndi Agiriki omwe, anamva mawu a Ambuye.

11 Mulungu anapitiriza kuchita zinthu zamphamvu komanso zodabwitsa kudzera mwa Paulo.+ 12 Moti anthu ankatenga ngakhale tinsalu ndi zovala* zimene zakhudza thupi la Paulo nʼkupita nazo kwa odwala,+ ndipo matenda awo ankatheratu. Nayonso mizimu yoipa inkatuluka.+ 13 Koma Ayuda ena amene ankayendayenda nʼkumatulutsa ziwanda, anayesa kutchula dzina la Ambuye Yesu pofuna kuchiritsa anthu amene anali ndi mizimu yoipa. Ankanena kuti: “Ndikukulamula mʼdzina la Yesu amene Paulo akumulalikira.”+ 14 Panali ana aamuna 7 a Sikeva, wansembe wamkulu wa Chiyuda, amene ankachita zimenezi. 15 Koma mzimu woipa unawayankha kuti: “Ine Yesu ndikumudziwa+ ndipo Paulo ndikumudziwanso bwino.+ Nanga inuyo ndinu ndani?” 16 Kenako, munthu amene anali ndi mzimu woipa uja anawalumphira. Analimbana nawo mmodzimmodzi mpaka kuwagonjetsa onsewo, moti anatuluka mʼnyumbamo nʼkuthawa ali maliseche komanso atavulala. 17 Anthu onse anadziwa zimenezi, Ayuda ndi Agiriki amene ankakhala ku Efeso. Choncho onse anagwidwa ndi mantha ndipo dzina la Ambuye Yesu linapitiriza kulemekezedwa. 18 Anthu ambiri amene anakhala okhulupirira ankabwera kudzaulula machimo awo ndiponso kufotokoza poyera zoipa zimene ankachita. 19 Anthu ambiri amene ankachita zamatsenga anasonkhanitsa mabuku awo nʼkuwatentha pamaso pa anthu onse.+ Ndipo atawerengera mtengo wake anapeza kuti anali okwana ndalama zasiliva zokwana 50,000. 20 Choncho mawu a Yehova* anapitiriza kufalikira ndipo sankagonjetseka.+

21 Zitachitika zimenezi, Paulo anatsimikiza mumtima mwake kupita ku Yerusalemu,+ kudzera ku Makedoniya+ ndi ku Akaya. Iye anati: “Ndikakafika kumeneko, ndikapitanso ku Roma.”+ 22 Choncho ku Makedoniya anatumizako awiri mwa anthu amene ankamutumikira, omwe ndi Timoteyo+ ndi Erasito.+ Koma iye anakhalabe mʼchigawo cha Asia kwa kanthawi ndithu.

23 Pa nthawiyo panayambika chisokonezo chachikulu+ chokhudza Njira ya Ambuye.+ 24 Panali munthu wina wosula siliva dzina lake Demetiriyo. Amisiri ankapindula kwambiri chifukwa cha ntchito yake yopanga tiakachisi tasiliva ta Atemi.+ 25 Demetiriyo anasonkhanitsa amisiriwo, limodzi ndi anthu ogwira ntchito yokhudza zinthu zimenezi. Ndiyeno anawauza kuti: “Anthu inu, mukudziwa kuti timapeza chuma kuchokera mu ntchito imeneyi. 26 Tsopano mukuona ndiponso mukumva zoti Paulo wakopa anthu ambiri kuti ayambe kukhulupirira zinthu zina. Wachita zimenezi osati mu Efeso+ mokha muno, koma pafupifupi mʼchigawo chonse cha Asia. Iye akumanena kuti milungu yopangidwa ndi manja si milungu ayi.+ 27 Ndipo chimene chikuopsa kwambiri si kunyozeka kwa ntchito yathu yokhayi, koma kachisi wa mulungu wamkulu wamkazi Atemi azidzaonedwa ngati wopanda pake. Mukudziwa kuti aliyense mʼchigawo chonse cha Asia komanso padziko lonse lapansi amalemekeza Atemi, koma chifukwa cha zimene Paulo akunena ulemerero wake udzatheratu.” 28 Atamva zimenezi anthuwo anakwiya kwambiri nʼkuyamba kufuula kuti: “Wamkulu ndi Atemi mulungu wa Aefeso!”

29 Zitatero mumzindawo munadzaza chisokonezo, ndipo anthu onse anathamangira mʼbwalo lamasewera, atagwira Gayo ndi Arisitako+ nʼkuwakokera mʼbwalomo. Gayo ndi Arisitako ankayenda ndi Paulo ndipo kwawo kunali ku Makedoniya. 30 Paulo ankafuna kulowa mkati mwa gulu la anthulo, koma ophunzira sanamulole. 31 Anthu ena oyangʼanira zikondwerero ndi masewera, amene anali anzake, nawonso anamutumizira uthenga womuchonderera kuti asaike moyo wake pachiswe pokalowa mʼbwalo lamaseweralo. 32 Kunena zoona, gulu lonselo linali litasokonezeka, ena ankafuula zina, ena zina. Moti ambiri sankadziwa nʼkomwe kuti nʼchifukwa chiyani asonkhana kumeneko. 33 Choncho iwo anatulutsa Alekizanda mʼgululo ndipo Ayuda anamukankhira kutsogolo. Kenako Alekizanda anakweza dzanja kuti alankhule podziteteza kwa anthuwo. 34 Koma iwo atazindikira kuti iye ndi Myuda, onse pamodzi anafuula kwa maola pafupifupi awiri kuti: “Wamkulu ndi Atemi mulungu wa Aefeso!”

35 Pamapeto pake, woyangʼanira mzinda atauza gulu la anthulo kuti likhale chete anati: “Anthu inu a mu Efeso, alipo kodi munthu amene sadziwa kuti mzinda wa Aefeso ndi umene umayangʼanira kachisi wa Atemi wamkulu ndi chifaniziro chimene chinagwa kuchokera kumwamba? 36 Popeza kuti palibe amene angatsutse zimenezi, muyenera kudekha, musachite zinthu mopupuluma. 37 Inu mwabweretsa anthu awa amene si akuba mu akachisi kapena onyoza mulungu wathu wamkaziyo. 38 Choncho ngati Demetiriyo+ ndi amisiri ali nawowa akuimba mlandu munthu, pamakhala masiku a milandu ndipo abwanamkubwa* alipo. Akasumirane kumeneko. 39 Koma ngati mukufuna zina zoposa pamenepa, chigamulo chake chiyenera kukaperekedwa pabwalo lovomerezeka. 40 Zimene zachitika lerozi nʼzoopsa chifukwa tingathe kuimbidwa nazo mlandu woukira boma. Palibiretu chifukwa chomveka chimene tingapereke pa chipolowe chimene chachitikachi.” 41 Atanena zimenezi, anauza anthuwo kuti achoke pamalowo.

20 Chipolowe chija chitatha, Paulo anaitanitsa ophunzira. Atawalimbikitsa nʼkutsanzikana nawo, ananyamuka ulendo wopita ku Makedoniya. 2 Iye anayendayenda mʼmadera akumeneko nʼkumalimbikitsa ophunzira ndi mawu ambiri, kenako anafika ku Girisi. 3 Atakhala kumeneko miyezi itatu, anaganiza zobwerera ku Makedoniya, chifukwa chakuti Ayuda+ anamukonzera chiwembu. Chiwembuchi anachikonza Paulo atangotsala pangʼono kuyamba ulendo wapamadzi wopita ku Siriya. 4 Pa ulendowu anali limodzi ndi Sopaturo mwana wa Puro wa ku Bereya, Arisitako+ ndi Sekundo a ku Tesalonika, Gayo wa ku Debe ndi Timoteyo,+ koma ochokera mʼchigawo cha Asia anali Tukiko+ ndi Terofimo.+ 5 Anthu amenewa anatsogola ndipo ankatiyembekezera ku Torowa. 6 Koma tinayamba ulendo wapanyanja ku Filipi masiku a Mkate Wopanda Zofufumitsa+ atatha. Ndipo tinawapeza ku Torowa patapita masiku 5. Kumeneko tinakhalako masiku 7.

7 Pa tsiku loyamba la mlungu, titasonkhana pamodzi kuti tidye chakudya, Paulo anayamba kuwakambira nkhani, chifukwa kunali koti anyamuka tsiku lotsatira. Ndipo analankhula kwa nthawi yaitali mpaka pakati pa usiku. 8 Mʼchipinda chamʼmwamba mmene tinasonkhanamo, munali nyale zambiri ndithu. 9 Paulo ali mkati mokamba nkhani, mnyamata wina dzina lake Utiko amene anakhala pawindo, anagona tulo tofa nato. Ali mʼtulo choncho, anagwa pansi kuchokera panyumba yachitatu yosanja, ndipo anamupeza atafa. 10 Koma Paulo anatsika pansi, ndipo anafika pamene iye anali nʼkumukumbatira.+ Kenako ananena kuti: “Khalani chete, chifukwa ali moyo tsopano.”+ 11 Atatero Paulo anapitanso mʼchipinda chamʼmwamba chija ndipo anatenga mkate nʼkuyamba kudya.* Anakambirana nawo kwa nthawi yaitali mpaka mʼbandakucha ndipo kenako ananyamuka nʼkumapita. 12 Choncho iwo anatenga mnyamata uja ali wamoyo ndipo anatonthozedwa kwambiri.

13 Tsopano ife tinatsogola kukakwera ngalawa nʼkuyamba ulendo wopita ku Aso. Iye anatiuza kuti titsogole ndipo tikamutengere ku Aso chifukwa ankafuna kuyenda wapansi. 14 Choncho atatipeza ku Aso, tinamukweza mʼngalawa nʼkupita ku Mitilene. 15 Mʼmawa wake titachoka kumeneko, tinafika pafupi ndi Kiyo. Koma tsiku lotsatira tinaima kwa kanthawi ku Samo, ndipo mʼmawa wake tinafika ku Mileto. 16 Paulo anaganiza zongolambalala Efeso,+ kuti asataye nthawi mʼchigawo cha Asia. Anachita zimenezi chifukwa ankafulumira kuti ngati nʼkotheka, pa tsiku la Chikondwerero cha Pentekosite akakhale ali ku Yerusalemu.+

17 Komabe ali ku Mileto anatumiza uthenga woti akulu a mpingo wa ku Efeso abwere. 18 Akuluwo atafika, iye anawauza kuti: “Inu mukudziwa bwino mmene ndinkachitira zinthu pa nthawi yomwe ndinali nanu, kuchokera tsiku limene ndinafika mʼchigawo cha Asia.+ 19 Ndinkatumikira Ambuye ngati kapolo modzichepetsa kwambiri,+ ndi misozi komanso ndi mayesero amene ndinakumana nawo chifukwa cha ziwembu za Ayuda. 20 Komatu sindinakubisireni chilichonse chothandiza ndipo sindinasiye kukuphunzitsani pagulu+ komanso kunyumba ndi nyumba.+ 21 Koma ndachitira umboni mokwanira kwa Ayuda ndi kwa Agiriki omwe, kuti alape+ nʼkubwerera kwa Mulungu komanso kuti ayambe kukhulupirira Ambuye wathu Yesu.+ 22 Ndipo tsopano, motsogoleredwa ndi mzimu, ndikupita ku Yerusalemu ngakhale kuti sindikudziwa zimene zikandichitikire kumeneko. 23 Koma chinthu chimodzi chokha chimene ndikudziwa nʼchakuti mumzinda ndi mzinda, mzimu woyera wandichitira umboni mobwerezabwereza kuti ndikuyembekezera kumangidwa komanso kuzunzidwa.+ 24 Komabe, moyo wanga sindikuuona ngati wofunika* kwa ine. Chimene ndikungofuna nʼchakuti ndimalize kuthamanga mpikisanowu, komanso kuti ndimalize+ utumiki umene ndinalandira kwa Ambuye Yesu. Ndikungofuna kuchitira umboni mokwanira za uthenga wabwino wa kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu.

25 Ndipo tamverani tsopano. Ndikudziwa kuti nonsenu amene ndinakulalikirani za Ufumu, simudzaonanso nkhope yanga. 26 Choncho mukhale mboni lero, kuti ine ndilibe mlandu wa magazi a anthu onse+ 27 chifukwa ndinakuuzani malangizo onse a Mulungu.*+ 28 Muzidziyangʼanira nokha+ komanso kusamalira gulu lonse la nkhosa, limene mzimu woyera wakuikani kuti muziliyangʼanira,+ kuti muwete mpingo wa Mulungu,+ umene anaugula ndi magazi a Mwana wake weniweni.+ 29 Ndikudziwa kuti ine ndikachoka, mimbulu yopondereza idzafika pakati panu+ ndipo sidzasamalira gulu la nkhosa mwachikondi. 30 Ndipo pakati panu anthu ena adzayamba kulankhula zinthu zopotoka kuti apatutse ophunzira aziwatsatira.+

31 Choncho khalani maso, ndipo muzikumbukira kuti kwa zaka zitatu+ masana ndi usiku, sindinasiye kuchenjeza aliyense wa inu ndikutulutsa misozi. 32 Koma tsopano ndikukusiyani kuti mutetezedwe ndi Mulungu ndiponso mawu a kukoma mtima kwake kwakukulu. Mawu amenewo angakulimbikitseni ndi kukupatsani cholowa pakati pa oyera onse.+ 33 Sindinasirire siliva, golide kapena chovala cha munthu.+ 34 Inunso mukudziwa bwino kuti manja awa anagwira ntchito kuti ndipeze zofunika pa moyo wanga+ ndi za amene ndinali nawo. 35 Pa zinthu zonse ndakusonyezani kuti pogwira ntchito molimbikira chonchi,+ muzithandiza ofooka ndipo muzikumbukira mawu a Ambuye Yesu. Paja iye anati, ‘Kupatsa kumatichititsa kukhala osangalala kwambiri+ kuposa kulandira.’”

36 Atanena zimenezi, iyeyo ndi akulu onsewo anagwada nʼkupemphera. 37 Zitatero onse analira kwambiri. Kenako anamuhaga* Paulo nʼkumukisa mwachikondi. 38 Iwo anamva chisoni kwambiri, makamaka chifukwa cha mawu amene iye ananena akuti sadzaonanso nkhope yake.+ Kenako anamʼperekeza kukakwera ngalawa.

21 Titadzikakamiza nʼkusiyana nawo, tinayamba ulendo wathu wapanyanja. Tinayenda osakhota mpaka kukafika ku Ko. Tsiku lotsatira tinafika ku Rode ndipo titachoka kumeneko tinakafika ku Patara. 2 Kumeneko tinapeza ngalawa imene inkawoloka kupita ku Foinike ndipo tinakwera nʼkunyamuka. 3 Chilumba cha Kupuro chitayamba kuonekera, tinachisiya kumanzere* nʼkupitiriza ulendo wathu kulowera ku Siriya. Kenako tinaima ku Turo kuti katundu atsitsidwe mʼngalawa. 4 Tinafufuza ophunzira ndipo titawapeza tinakhala nawo masiku 7. Koma mouziridwa ndi mzimu, iwo anauza Paulo mobwerezabwereza kuti asayerekeze kupita ku Yerusalemu.+ 5 Masiku athu okhala kumeneko atatha, tinanyamuka kuti tipitirize ulendo wathu. Abale onse komanso azimayi ndi ana, anatiperekeza mpaka kunja kwa mzindawo. Kumeneko tinagwada mʼmbali mwa nyanja nʼkupemphera. 6 Kenako tinatsanzikana ndipo ife tinakwera ngalawa, koma iwo anabwerera kunyumba kwawo.

7 Choncho tinanyamuka ku Turo pangalawa ndipo tinafika ku Tolemayi. Kumeneko tinapereka moni kwa abale nʼkukhala nawo tsiku limodzi. 8 Tsiku lotsatira tinanyamuka nʼkukafika ku Kaisareya ndipo tinapita kunyumba kwa mlaliki wina dzina lake Filipo. Iyeyu anali mmodzi wa amuna 7+ a mbiri yabwino aja, ndipo tinakhala naye. 9 Filipo anali ndi ana aakazi 4 osakwatiwa,* amene ankanenera.+ 10 Koma titakhala masiku ndithu, mneneri wina dzina lake Agabo+ anabwera kuchokera ku Yudeya. 11 Iye anafika kwa ife nʼkutenga lamba wa Paulo. Kenako anadzimanga mapazi ndi manja nʼkunena kuti: “Mzimu woyera wati, ‘Mwiniwake wa lambayu, Ayuda adzamumanga chonchi ku Yerusalemu+ nʼkumupereka kwa anthu a mitundu ina.’”+ 12 Titamva zimenezi, ife ndi anthu amene anali kumeneko, tinayamba kuchonderera Paulo kuti asapite ku Yerusalemu. 13 Koma Paulo anayankha kuti: “Nʼchifukwa chiyani mukulira ndiponso kufuna kundifooketsa? Inetu ndine wokonzeka osati kumangidwa kokha, komanso kukafa ku Yerusalemu chifukwa cha dzina la Ambuye Yesu.”+ 14 Titalephera kumusintha maganizo, tinasiya kumuletsa* nʼkunena kuti: “Chifuniro cha Yehova* chichitike.”

15 Kenako tinakonzeka nʼkunyamuka ulendo wopita ku Yerusalemu. 16 Koma ophunzira ena a ku Kaisareya ananyamuka nafe kuti atiperekeze kunyumba kwa Mnaso wa ku Kupuro, kuti tikafikire kumeneko. Munthu ameneyu anali mmodzi wa ophunzira oyambirira. 17 Titafika ku Yerusalemu, abale anatilandira mosangalala. 18 Koma tsiku lotsatira, Paulo anapita nafe kwa Yakobo,+ ndipo akulu onse anali komweko. 19 Paulo anawapatsa moni nʼkuyamba kuwafotokozera mwatsatanetsatane zimene Mulungu anachitira anthu a mitundu ina kudzera mu utumiki wake.

20 Iwo atamva zimenezi anayamba kutamanda Mulungu, komabe anamuuza kuti: “Mʼbale, pali Ayuda ambiri okhulupirira ndipo onsewa ndi odzipereka pa nkhani yotsatira Chilamulo.+ 21 Komatu iwo anamva mphekesera zakuti iwe wakhala ukuphunzitsa Ayuda onse amene ali pakati pa anthu a mitundu ina kuti asiye kutsatira Chilamulo cha Mose. Akuti ukuwauza kuti asamachitenso mdulidwe wa ana awo komanso asamatsatire miyambo imene takhala tikuitsatira kuyambira kalekale.+ 22 Ndiye titani pamenepa? Sitikukayikira kuti iwo adzamva kuti iwe wabwera. 23 Choncho uchite zimene tikuuze: Tili ndi amuna 4 amene anachita lumbiro. 24 Utenge anthu amenewa ndipo ukachite nawo mwambo wa kudziyeretsa. Uwalipirire zonse zofunika, kuti amete tsitsi lawo. Ukatero, aliyense adziwa kuti mphekesera zimene anamva za iwe ndi nkhambakamwa chabe. Adzaona kuti ukuchita zinthu motsatira dongosolo komanso kuti umasunga Chilamulo.+ 25 Koma okhulupirira ochokera mʼmitundu inawo, tinawatumizira kalata yonena za chigamulo chathu chakuti apewe zoperekedwa nsembe kwa mafano+ komanso magazi,+ zopotola*+ ndi chiwerewere.”*+

26 Choncho tsiku lotsatira, Paulo anatenga amunawo nʼkukachita nawo mwambo wa kudziyeretsa.+ Kenako analowa mʼkachisi, kukanena pamene masiku awo a mwambo wa kudziyeretsa adzathere ndiponso pamene adzapereke nsembe ya aliyense.

27 Masiku 7 atatsala pangʼono kutha, Ayuda ochokera ku Asia anaona Paulo ali mʼkachisi. Choncho anachititsa kuti pagulu lonse la anthu payambike chisokonezo ndipo anamugwira. 28 Iwo ankafuula kuti: “Inu Aisiraeli, tithandizeni! Munthu uyu akuphunzitsa zotsutsana ndi anthu a mtundu wathu kulikonse. Iyeyu akuphunzitsanso zotsutsana ndi Chilamulo komanso malo ano. Kuwonjezera pamenepo, watenga Agiriki nʼkuwalowetsa mʼkachisi ndipo waipitsa malo oyerawa.”+ 29 Iwo ananena zimenezi chifukwa tsiku lina anaona Terofimo+ wa ku Efeso ali naye limodzi mumzindawo ndiye anaganiza kuti Paulo analowetsa Terofimo mʼkachisi. 30 Choncho mumzinda wonsewo munali chisokonezo ndipo anthu anathamangira kukachisiko. Kenako anagwira Paulo nʼkumukokera kunja kwa kachisi. Nthawi yomweyo zitseko zinatsekedwa. 31 Pamene ankafuna kumupha, uthenga unafika kwa mkulu wa gulu la asilikali kuti mu Yerusalemu monse muli chisokonezo. 32 Nthawi yomweyo, iye anatenga asilikali ndi atsogoleri awo nʼkuthamangira kumeneko. Anthuwo ataona mkulu wa asilikali uja pamodzi ndi asilikali akewo, anasiya kumenya Paulo.

33 Zitatero mkulu wa asilikaliyo anafika pafupi nʼkumugwira ndipo analamula kuti amumange ndi maunyolo awiri.+ Kenako anafunsa anthu zokhudza iyeyo komanso zimene wachita. 34 Koma ena pagululo anayamba kufuula zinthu zina, ena zina. Choncho atalephera kutolapo mfundo yeniyeni chifukwa cha phokoso, analamula kuti apite naye kumpanda wa asilikali. 35 Atafika pamasitepe, asilikaliwo anachita kumunyamula chifukwa choti gululo linkachita zachiwawa. 36 Anthuwo ankawatsatira, akufuula kuti: “Aphedwe ameneyo!”

37 Koma atatsala pangʼono kulowa naye kumpanda wa asilikali, Paulo anapempha mkulu wa asilikali kuti: “Kodi mungandilole kuti ndilankhule nanu pangʼono?” Iye anati: “Kani umalankhula Chigiriki? 38 Ndiye kuti si iwe munthu wa ku Iguputo amene masiku apitawo unayambitsa chipolowe choukira boma nʼkutsogolera zigawenga 4,000 kupita nazo mʼchipululu?” 39 Paulo anayankha kuti: “Inetu ndine Myuda+ wa ku Tariso,+ ku Kilikiya, nzika ya mzinda wotchuka. Chonde ndikukupemphani, ndiloleni ndilankhule kwa anthuwa.” 40 Atamulola, Paulo anaimirira pamasitepe nʼkukwezera anthuwo dzanja. Onse atakhala chete, analankhula nawo mʼChiheberi+ kuti:

22 “Anthu inu, abale anga ndi abambo anga, mvetserani mawu anga odziteteza.”+ 2 Atamva kuti akulankhula nawo mʼChiheberi, onse anangoti zii, ndipo iye anati: 3 “Inetu ndine Myuda,+ wobadwira ku Tariso wa ku Kilikiya,+ koma ndinaphunzitsidwa ndi Gamaliyeli+ mumzinda womwe uno. Anandiphunzitsa kutsatira kwambiri Chilamulo cha makolo+ athu. Ndipo ndinali wodzipereka potumikira Mulungu ngati mmene nonsenu mulili lero.+ 4 Ndinkazunza otsatira Njira imeneyi mpaka kuwapha. Ndinkamanga amuna ndi akazi nʼkukawapereka kundende.+ 5 Ndipotu mkulu wa ansembe ndi bungwe lonse la akulu angandichitire umboni. Kwa amenewa nʼkumene ndinapezanso makalata ondiloleza kuti ndikamange abale ku Damasiko. Ndinanyamuka kuti ndikagwire anthu omwe anali kumeneko nʼkuwabweretsa ku Yerusalemu atamangidwa kuti adzapatsidwe chilango.

6 Koma ndili mʼnjira, nditatsala pangʼono kufika ku Damasiko, dzuwa lili pamutu, mwadzidzidzi kunawala kwambiri. Kuwala kumeneku kunali kochokera kumwamba ndipo kunazungulira pamene ine ndinali.+ 7 Ndinagwa pansi ndipo ndinamva mawu akuti: ‘Saulo! Saulo! Nʼchifukwa chiyani ukundizunza?’ 8 Ine ndinayankha kuti, ‘Ndinu ndani Mbuyanga?’ Ndipo anandiuza kuti, ‘Ndine Yesu wa ku Nazareti, amene iwe ukumuzunza.’ 9 Amuna amene ndinali nawo anaona kuwalako, koma sanamvetse mawu amene ankalankhula ndi inewo. 10 Ndiye ine ndinati, ‘Nditani Ambuye?’ Ambuyewo anandiuza kuti, ‘Nyamuka ndipo upite ku Damasiko. Kumeneko ukauzidwa zonse zimene zakonzedwa kuti uchite.’+ 11 Koma popeza sindinkatha kuona chilichonse chifukwa cha ulemerero wa kuwalako, anthu amene ndinali nawo aja, anandigwira dzanja mpaka kukafika ku Damasiko.

12 Ndiyeno Hananiya, munthu woopa Mulungu mogwirizana ndi Chilamulo, amene anali ndi mbiri yabwino pakati pa Ayuda onse akumeneko, 13 anabwera. Iye anaima chapafupi nʼkunena kuti: ‘Mʼbale wanga Saulo, yambanso kuona!’ Nthawi yomweyo ndinakweza maso anga nʼkumuona.+ 14 Ndiyeno iye anati: ‘Mulungu wa makolo athu wakusankha kuti udziwe chifuniro chake, uone wolungamayo+ ndiponso umve mawu apakamwa pake. 15 Chifukwa udzakhala mboni yake kwa anthu onse pa zinthu zimene waona komanso kumva.+ 16 Ndiye ukuchedweranji? Nyamuka ubatizidwe nʼkuchotsa machimo ako+ poitanira pa dzina lake.’+

17 Koma nditabwerera ku Yerusalemu+ nʼkuyamba kupemphera mʼkachisi, ndinaona masomphenya. 18 Mʼmasomphenyawo ndinaona Ambuye akundiuza kuti, ‘Tuluka mu Yerusalemu mwamsanga, chifukwa iwo sadzamva uthenga wako wonena za ine.’+ 19 Ndipo ine ndinanena kuti, ‘Ambuye, iwowo akudziwa bwino kuti ndinkapita mʼmasunagoge nʼkumatsekera mʼndende ndiponso kukwapula anthu amene ankakukhulupirirani.+ 20 Komanso pamene Sitefano, mboni yanu ankaphedwa, ine ndinali pomwepo ndipo ndinavomereza. Ndi inenso amene ndinkayangʼanira malaya akunja a anthu amene ankamuphawo.’+ 21 Koma anandiuzabe kuti, ‘Nyamuka, chifukwa ndidzakutumiza kutali kwa anthu a mitundu ina.’”+

22 Iwo ankamumvetsera mpaka pa mawu amenewa. Koma kenako anafuula kuti: “Munthu ameneyu asapezekenso padziko lapansi! Sakuyenera kukhala ndi moyo!” 23 Koma popeza ankafuula komanso kuponya mʼmwamba malaya awo akunja ndi fumbi,+ 24 mkulu wa asilikali analamula kuti alowe naye kumpanda wa asilikali. Iye anati ayenera kumufunsa mafunso kwinaku akumʼkwapula kuti adziwe chimene chachititsa kuti anthu azimukuwiza* choncho. 25 Koma atamugoneka kuti amukwapule, Paulo anafunsa mtsogoleri wa asilikali amene anaima pamenepo kuti: “Kodi malamulo amakulolani kukwapula nzika ya Roma mlandu wake usanazengedwe?”+ 26 Mtsogoleri wa asilikaliyo atamva zimenezi, anapita kwa mkulu wa asilikali nʼkukamuuza kuti: “Mukufuna kuchita chiyani? Munthuyutu ndi nzika ya Roma.” 27 Zitatero mkulu wa asilikaliyo anabwera nʼkunena kuti: “Tandiuza, kodi nʼzoona kuti ndiwe nzika ya Roma?” Iye anati: “Inde.” 28 Mkulu wa asilikaliyo anati: “Ine ndinagula ufulu wokhala nzika ndi ndalama zambiri.” Paulo anati: “Koma ine wanga ndinachita kubadwa nawo.”+

29 Nthawi yomweyo amuna amene ankafuna kumufunsa mafunso, uku akumukwapula, anachoka nʼkumusiya. Nayenso mkulu wa asilikali uja anachita mantha atadziwa kuti munthu amene anamumangayo ndi nzika ya Roma.+

30 Tsiku lotsatira, pofuna kudziwa chenicheni chimene Ayudawo ankamuimbira mlandu, anamutulutsa. Atatero analamula ansembe aakulu ndi Khoti Lalikulu la Ayuda kuti asonkhane. Ndiyeno anabweretsa Paulo nʼkumuimika pakati pawo.+

23 Paulo anayangʼanitsitsa Khoti Lalikulu la Ayudalo nʼkunena kuti: “Anthu inu, abale anga, ndachita zinthu popanda chikumbumtima changa kunditsutsa ngakhale pangʼono pamaso pa Mulungu+ mpaka lero.” 2 Hananiya mkulu wa ansembe atamva zimenezi, analamula anthu amene anaimirira pafupi naye kuti amʼmenye pakamwa. 3 Atatero, Paulo anamuuza kuti: “Uona, Mulungu akulanga, khoma lopaka laimu iwe. Wakhala pamenepo kuti undiweruze motsatira Chilamulo, ndiye ukuphwanyanso Chilamulocho polamula kuti andimenye?” 4 Anthu amene anaima naye pafupi anati: “Kodi ukunyoza mkulu wa ansembe wa Mulungu?” 5 Paulo anati: “Abale, sindinadziwe kuti ndi mkulu wa ansembe. Chifukwa Malemba amati, ‘Wolamulira wa anthu a mtundu wako usamunenere zachipongwe.’”+

6 Paulo ataona kuti ena a iwo anali Asaduki ndipo ena anali Afarisi, anafuula mʼkhotimo kuti: “Anthu inu, abale anga, ine ndine Mfarisi,+ mwana wa Afarisi. Pano ndikuweruzidwa chifukwa cha chiyembekezo chakuti akufa adzauka.” 7 Atanena zimenezi, Afarisi ndi Asaduki anayamba kukangana kwambiri, ndipo gululo linagawanika. 8 Chifukwa Asaduki amanena kuti munthu wakufa sangauke komanso kulibe angelo kapena cholengedwa chauzimu. Pomwe Afarisi amavomereza poyera kuti zonsezi zilipo.+ 9 Choncho panali chiphokoso, ndipo alembi ena a gulu la Afarisi anaimirira nʼkuyamba kutsutsa mwaukali kuti: “Sitikupeza chimene munthuyu walakwa. Koma ngati mzimu kapena mngelo walankhula naye+ . . .” 10 Mkanganowo utakula kwambiri, mkulu wa asilikali anachita mantha kuti anthuwo amukhadzulakhadzula Paulo. Choncho analamula asilikali kuti apite akamuchotse pagululo nʼkubwera naye kumpanda wa asilikali.

11 Koma usiku wa tsiku lomwelo, Ambuye anaima pafupi ndi Paulo nʼkumuuza kuti: “Limba mtima.+ Chifukwa wandichitira umboni mokwanira ku Yerusalemu, ndipo ukandichitiranso umboni ku Roma.”+

12 Kutacha, Ayuda anakonza chiwembu nʼkulumbira pochita kudzitemberera kuti saadya kapena kumwa chilichonse mpaka atapha Paulo. 13 Panali amuna oposa 40 amene anakonza chiwembu chochita kulumbirirachi. 14 Anthuwa anapita kwa ansembe aakulu ndi akulu kukanena kuti: “Ife talumbira pochita kudzitemberera kuti sitidya chilichonse mpaka titapha Paulo. 15 Tsopano inuyo ndi Khoti Lalikulu la Ayuda, muuze mkulu wa asilikali kuti abweretse Paulo kwa inu ngati kuti mukufuna kumvetsa bwino nkhani yake. Koma asanafike ife tidzamupha.”

16 Koma mwana wamwamuna wa mchemwali wake wa Paulo anamva kuti anthuwo akonza zokamudikirira panjira, ndipo anapita kumpanda wa asilikali nʼkukamuuza Paulo zimenezi. 17 Choncho Paulo anaitana mmodzi wa atsogoleri a asilikali nʼkumuuza kuti: “Mʼtenge mnyamatayu upite naye kwa mkulu wa asilikali chifukwa ali ndi mawu oti akamuuze.” 18 Choncho anamutengadi nʼkupita naye kwa mkulu wa asilikali ndipo ananena kuti: “Paulo, mkaidi uja, anandiitana nʼkundiuza kuti ndimubweretse mnyamatayu. Akuti ali ndi mawu oti akuuzeni.” 19 Mkulu wa asilikaliyo anamugwira dzanja mnyamatayo nʼkupita naye pambali ndipo anamufunsa kuti: “Ukufuna kundiuza chiyani?” 20 Iye anati: “Ayuda agwirizana zoti akupempheni kuti mawa mupititse Paulo kubwalo la Khoti Lalikulu la Ayuda, ngati kuti akufuna kumvetsa bwino mlandu wake.+ 21 Koma musalole kuti akunyengerereni, chifukwa amuna oposa 40 akufuna kudzamudikirira panjira. Anthu amenewa alumbira mochita kudzitemberera kuti saadya kapena kumwa chilichonse mpaka atamupha.+ Moti panopa akonzeka, akungoyembekezera chilolezo chanu.” 22 Mkulu wa asilikaliyo anauza mnyamatayo kuti azipita atamulangiza kuti: “Usauze aliyense kuti wandifotokozera zimenezi.”

23 Ndiyeno anaitanitsa atsogoleri awiri a asilikali nʼkuwauza kuti: “Uzani asilikali 200 kuti akonzekere kuyenda ulendo wopita ku Kaisareya cha mʼma 9 koloko* usiku uno. Pakhalenso amuna 70 okwera pamahatchi* ndiponso asilikali 200 a mikondo. 24 Muwapatsenso mahatchi oti akwezepo Paulo kuti akafike kwa bwanamkubwa Felike ali wotetezeka.” 25 Ndiyeno iye analemba kalata yonena kuti:

26 “Ine Kalaudiyo Lusiya, ndikulembera inu Wolemekezeka Bwanamkubwa Felike: Landirani moni! 27 Munthu uyu anagwidwa ndi Ayuda ndipo anatsala pangʼono kumupha. Koma nthawi yomweyo ndinafika ndi gulu langa la asilikali nʼkumupulumutsa,+ chifukwa ndinamva kuti iyeyu ndi nzika ya Roma.+ 28 Ndiyeno pofuna kudziwa chimene anapalamula, ndinapita naye ku Khoti Lalikulu la Ayuda.+ 29 Kumeneko ndinapeza kuti akumuimba mlandu pa nkhani zokhudza Chilamulo chawo.+ Koma sanapezeke ndi mlandu uliwonse woyenera kuphedwa kapena kutsekeredwa mʼndende. 30 Komabe popeza ndadziwa chiwembu chimene amukonzera munthuyu,+ ndamutumiza kwa inu, ndipo ndalamula omuimba mlanduwo kuti adzanene mlandu wake pamaso panu.”

31 Choncho asilikaliwo anatenga Paulo+ usiku nʼkupita naye ku Antipatiri mogwirizana ndi zimene anawalamula. 32 Tsiku lotsatira anasiya amuna okwera pamahatchi aja kuti apitirire naye, koma iwo anabwerera kumpanda wa asilikali. 33 Amuna okwera pamahatchiwo anafika ku Kaisareya nʼkupereka kalata ija kwa bwanamkubwa ndipo anaperekanso Paulo. 34 Choncho bwanamkubwayo anawerenga kalatayo ndipo anafunsa chigawo chimene Paulo ankachokera. Anamva kuti ankachokera ku Kilikiya.+ 35 Ndiyeno anati: “Ndimvetsera mlandu wako wonse anthu okuimba mlanduwo akafika.”+ Ndipo analamula kuti amusunge mʼnyumba ya Mfumu Herode nʼkumamulondera.

24 Patatha masiku 5, kunafika mkulu wa ansembe Hananiya+ pamodzi ndi akulu ena, komanso munthu wina wodziwa kulankhula,* dzina lake Teritulo. Iwo anayamba kufotokoza mlandu wa Paulo kwa bwanamkubwa.+ 2 Teritulo atapatsidwa mwayi kuti alankhule, anayamba kumuneneza Paulo kuti:

“Tili pa mtendere wambiri chifukwa cha inu, komanso zinthu zikusintha mu mtundu wathuwu chifukwa cha nzeru zanu zoona patali. 3 Choncho nthawi zonse komanso kulikonse, inu Wolemekezeka a Felike, ife timaona nzeru zanuzo ndipo timayamikira kwambiri. 4 Koma kuti ndisakutayitseni nthawi, ndikupempha kuti mutikomere mtima ndipo mumve mawu athu pangʼono. 5 Ife tapeza kuti munthu uyu ndi wovutitsa kwabasi,+ ndipo akuyambitsa zoukira boma+ pakati pa Ayuda padziko lonse. Ndiponso ndi mtsogoleri wa gulu lampatuko la anthu a ku Nazareti.+ 6 Komanso iyeyu ankafuna kudetsa kachisi ndipo tinamugwira.+ 7*⁠—— 8 Mutamufunsa, mungathe kutsimikizira nokha zonse zimene tikunenazi.”

9 Atanena zimenezi Ayuda nawonso analowerera ndipo ankanena motsimikiza kuti zimenezo nʼzoona. 10 Bwanamkubwayo atagwedezera Paulo mutu kuti alankhule, Paulo anayankha kuti:

“Ndikudziwa kuti mwakhala woweruza wa mtundu uwu kwa zaka zambiri. Choncho ndine wosangalala kulankhula podziteteza pa zimene akundinenerazi.+ 11 Inu mukhoza kupeza umboni wakuti masiku 12 sanadutse kuchokera pamene ine ndinapita ku Yerusalemu+ kukalambira Mulungu. 12 Ndipo iwowa sanandipezepo mʼkachisi ndikutsutsana ndi aliyense. Sanandipezenso ndikuyambitsa chipolowe mʼmasunagoge kapena pena paliponse mumzindawu. 13 Ndipo panopa sangathe kukupatsani umboni wa zimene akundinenerazi. 14 Koma chomwe ndikuvomereza kwa inu ndi chakuti: Njira yolambirira imene iwo akuitchula kuti ‘gulu lampatuko,’ ndi imene ine ndikuitsatira potumikira Mulungu wa makolo anga.+ Chifukwa ndimakhulupirira zonse zimene zili mʼChilamulo ndi zimene aneneri analemba.+ 15 Ndipo ine ndili ndi chiyembekezo ngati chimenenso anthu awa ali nacho, kuti Mulungu adzaukitsa+ olungama ndi osalungama omwe.+ 16 Chifukwa cha zimenezi, ndikuyesetsa mwakhama kuti ndikhale ndi chikumbumtima chabwino kwa Mulungu ndiponso kwa anthu.+ 17 Ndiyeno pambuyo pa zaka zambiri, ndinabwera kudzapereka mphatso zachifundo+ kwa anthu a mtundu wanga ndiponso kudzapereka nsembe. 18 Pamene ndinkachita zimenezi, anandipeza mʼkachisi nditadziyeretsa motsatira mwambo.+ Panalibe gulu la anthu kapena phokoso, koma panali Ayuda ena ochokera mʼchigawo cha Asia. 19 Amenewo, akanakhala ndi chifukwa, ndi amene anayenera kubwera kwa inu kudzandiimba mlandu.+ 20 Kapena muwalole anthu ali panowa, afotokoze okha ngati anandipeza ndi mlandu uliwonse pamene ndinaima pamaso pa Khoti Lalikulu la Ayuda. 21 Mawu amodzi okha amene ine ndinanena, pamene ndinaima pakati pawo ndi akuti, ‘Ine lero ndikuweruzidwa chifukwa cha chiyembekezo chakuti akufa adzauka!’”+

22 Popeza Felike ankadziwa bwino nkhani yokhudza Njira imeneyi,+ anaimitsa mlanduwo nʼkunena kuti: “Ndidzagamula mlandu wanuwu akadzafika Lusiya mkulu wa asilikali.” 23 Iye analamula mtsogoleri wa asilikali kuti amusunge mʼndende, koma amupatseko ufulu ndipo azilola anthu a mtundu wake kudzamuthandiza.

24 Patapita masiku angapo, Felike anafika pamodzi ndi mkazi wake Durusila, amene anali Myuda. Ndiyeno Felike anaitanitsa Paulo nʼkumamvetsera pamene ankafotokoza za kukhulupirira Khristu Yesu.+ 25 Koma pamene ankafotokoza zokhudza chilungamo, kudziletsa ndiponso chiweruzo chimene chikubwera,+ Felike anachita mantha ndipo anati: “Basi pita kaye, ndikadzapeza nthawi ndidzakuitananso.” 26 Komanso ankaganiza kuti Paulo amupatsa ndalama. Choncho ankamuitanitsa pafupipafupi nʼkumakambirana naye. 27 Patatha zaka ziwiri, Felike analowedwa mʼmalo ndi Porikiyo Fesito. Koma popeza Felike ankafuna kuti Ayuda azimukonda,+ anangomusiya Paulo mʼndende.

25 Patatha masiku atatu kuchokera pamene Fesito+ anafika mʼchigawocho nʼkuyamba kulamulira, anapita ku Yerusalemu kuchokera ku Kaisareya. 2 Kumeneko ansembe aakulu ndi amuna olemekezeka pakati pa Ayuda anamuuza zinthu zoipa zokhudza Paulo.+ Ndiyeno anayamba kumuchonderera 3 kuti awakomere mtima nʼkuitanitsa Paulo kuti abwere ku Yerusalemu. Koma anakonza zoti amudikirire panjira nʼkumupha.+ 4 Koma Fesito anawayankha kuti Paulo akuyenera kusungidwa ku Kaisareya ndiponso kuti iyeyo watsala pangʼono kubwerera komweko. 5 Ndiyeno anati: “Amene ali ndi maudindo pakati panu, tipitire limodzi kuti ngati pali chilichonse chimene munthu ameneyu walakwa akamuimbe mlandu.”+

6 Choncho iye atakhala nawo kumeneko kwa masiku osapitirira 8 kapena 10, anabwerera ku Kaisareya. Ndipo tsiku lotsatira anakhala pampando woweruzira milandu nʼkuuza anthu kuti abweretse Paulo. 7 Paulo atafika, Ayuda amene anabwera kuchokera ku Yerusalemu, anaima momuzungulira nʼkumamuneneza milandu yambiri yoopsa, imene sanathe kupereka umboni wake.+

8 Koma Paulo podziteteza anati: “Ine sindinachimwire Chilamulo cha Ayuda kapena kachisi kapenanso Kaisara.”+ 9 Koma pofuna kuti Ayudawo amukonde,+ Fesito anafunsa Paulo kuti: “Kodi ukufuna kupita ku Yerusalemu kuti nkhaniyi ikaweruzidwe kumeneko pamaso panga?” 10 Koma Paulo anayankha kuti: “Ine ndaima kutsogolo kwa mpando woweruzira milandu wa Kaisara, kumene ndiyenera kuweruzidwa. Ayuda sindinawalakwire chilichonse ngati mmene inunso mukuonera. 11 Ngati ndilidi wolakwa, ndipo ndikuyenera kuphedwa chifukwa cha zimene ndachita,+ sindikukana kufa. Koma ngati zimene akundinenezazi ndi zosamveka, palibe munthu amene angandipereke kwa iwo kuti awasangalatse. Ndikuchita apilo kuti ndikaonekere kwa Kaisara.”+ 12 Ndiyeno Fesito atakambirana ndi aphungu, anayankha kuti: “Popeza wachita apilo kuti ukaonekere kwa Kaisara, udzapitadi kwa Kaisara.”

13 Patatha masiku angapo, Mfumu Agiripa ndi Berenike anafika ku Kaisareya pa ulendo wa boma wokapereka ulemu kwa Fesito. 14 Popeza anakhala kumeneko masiku angapo, Fesito anafotokozera mfumuyo nkhani yokhudza Paulo. Iye anati:

“Pali munthu wina amene Felike anamusiya mʼndende. 15 Pamene ndinali ku Yerusalemu, ansembe aakulu komanso akulu a Ayuda anabwera kudzandiuza zoipa zokhudza iyeyu+ ndipo anapempha chiweruzo choti aphedwe. 16 Koma ine ndinawayankha kuti Aroma sachita zinthu mʼnjira imeneyo. Iwo sapereka munthu kwa anthu omuneneza pongofuna kuwasangalatsa, munthu wonenezedwayo asanapatsidwe mwayi woonana pamasomʼpamaso ndi omunenezawo kuti adziteteze pa mlanduwo.+ 17 Choncho atafika kuno, sindinachedwe, koma tsiku lotsatira ndinakhala pampando woweruzira milandu nʼkuitanitsa munthuyo kuti abwere naye. 18 Omunenezawo ataima nʼkuyamba kufotokoza, sanatchule zoipa zilizonse zimene ndinkaganiza kuti munthuyu anachita.+ 19 Iwo ankangotsutsana naye nkhani zokhudza mmene amalambirira mulungu*+ komanso za munthu wina dzina lake Yesu amene anafa, koma Paulo akunenabe motsimikiza kuti ali moyo.+ 20 Nditalephera kuthetsa mkangano wa nkhani zimenezi, ndinamufunsa ngati akufuna kupita ku Yerusalemu kuti akaweruzidwe kumeneko.+ 21 Koma Paulo anapempha kuti timusunge kuti akamve chigamulo cha Wolemekezeka.+ Choncho ndinalamula kuti asungidwe mpaka pamene ndidzamutumize kwa Kaisara.”

22 Agiripa anauza Fesito kuti: “Inenso ndikufuna ndimve ndekha munthu ameneyu akulankhula.”+ Iye anati: “Mawa mudzamumvetsera.” 23 Tsiku lotsatira, Agiripa ndi Berenike anabwera ndi ulemu waukulu wachifumu nʼkulowa mʼchipinda chimene anthu ankasonkhana. Anali ndi akuluakulu a asilikali komanso anthu otchuka amumzindawo ndipo Fesito atalamula, anabweretsa Paulo. 24 Ndiyeno Fesito ananena kuti: “Mfumu Agiripa ndi anthu nonse amene muli nafe pano, mwamuona munthuyu? Ayuda onse ku Yerusalemu komanso kuno, anandipempha kuti iyeyu sakuyeneranso kukhala ndi moyo ndipo analankhula zimenezi mofuula.+ 25 Koma ine ndinaona kuti sanachite chilichonse choyenera kuphedwa.+ Choncho iyeyu atapempha kuti akaonekere kwa Wolemekezeka, ndinaganiza zomutumiza. 26 Koma ndilibe mfundo iliyonse imene ndingalembere Mbuyanga yokhudza munthuyu. Choncho ndamubweretsa kwa nonsenu, makamaka inu Mfumu Agiripa, kuti mukamufunsa za nkhaniyi, ndipeze cholemba. 27 Chifukwa ine ndikuona kuti si nzeru kutumiza mkaidi, koma osatchula milandu yake.”

26 Agiripa+ anauza Paulo kuti: “Ukhoza kulankhula mbali yako.” Ndiyeno Paulo anakweza dzanja nʼkuyamba kulankhula modziteteza kuti:

2 “Inu Mfumu Agiripa, ndine wosangalala kuti lero ndidziteteza pamaso panu, pa zinthu zonse zimene Ayuda akundineneza.+ 3 Makamaka chifukwa chakuti ndinu katswiri pa miyambo yonse komanso pa zimene Ayuda amakangana. Choncho ndikukupemphani kuti mundimvetsere moleza mtima.

4 Ndithudi, moyo umene ndakhala kuyambira ndili mnyamata, pakati pa anthu a mtundu wanga ndiponso mu Yerusalemu, ndi wodziwika bwino kwa Ayuda onse+ 5 amene akundidziwa kuyambira kale. Atafuna, angandichitire umboni kuti ndinalidi Mfarisi+ wa mʼgulu limene limalambira mokhwimitsa zinthu kwambiri.+ 6 Koma tsopano ndikuimbidwa mlandu chifukwa cha chiyembekezo cha zimene Mulungu analonjeza makolo athu.+ 7 Mafuko athu 12 akuyembekezera kuona kukwaniritsidwa kwa lonjezo limeneli ndipo akumuchitira Mulunguyo utumiki wopatulika mosalekeza masana ndi usiku. Choncho Mfumu, Ayuda akundiimba mlandu chifukwa cha chiyembekezo chimenechi.+

8 Nʼchifukwa chiyani anthu inu mukuona kuti nʼzosatheka kuti Mulungu aukitse akufa? 9 Inetu ndinkaganiza kuti ndiyenera kuchita zambiri zotsutsana ndi dzina la Yesu wa ku Nazareti. 10 Ndipo izi ndi zimene ndinachitadi ku Yerusalemu. Ndinkatsekera mʼndende oyera ambiri+ nditapatsidwa mphamvu ndi ansembe aakulu.+ Akaweruzidwa kuti aphedwe, ine ndinkavomereza. 11 Nthawi zambiri ndinkawapatsa chilango mʼmasunagoge onse, pofuna kuwakakamiza kuti asiye zimene amakhulupirira. Popeza ndinali nditakwiya nawo kwambiri, ndinafika powazunza ngakhale mʼmizinda yakunja.

12 Ndili ndi zolinga zimenezi, ndinanyamuka ulendo wopita ku Damasiko nditapatsidwa mphamvu komanso chilolezo ndi ansembe aakulu. 13 Koma ndili mʼnjira dzuwa lili pamutu, inu mfumu, ndinaona kuwala kochokera kumwamba koposa kuwala kwa dzuwa ndipo kunandizungulira ineyo ndiponso anthu amene ndinali nawo pa ulendowu.+ 14 Ndiyeno tonse titagwa pansi, ndinamva mawu akundiuza mʼChiheberi kuti, ‘Saulo! Saulo! Nʼchifukwa chiyani ukundizunza? Ukungovutika popitiriza kuchita ngati nyama imene ikuponya miyendo yake nʼkumamenya zisonga zotosera.’* 15 Koma ine ndinati: ‘Ambuye, ndinu ndani kodi?’ Ndipo Ambuye anati: ‘Ndine Yesu amene iwe ukumuzunza. 16 Komabe dzuka ndipo uimirire. Ndaonekera kwa iwe kuti ndikusankhe kuti ukhale mtumiki komanso mboni ya zinthu zonse zokhudza ine, zomwe waona ndiponso zimene ndidzakuonetsa.+ 17 Ndipo ndidzakupulumutsa kwa anthu awa komanso kwa anthu a mitundu ina kumene ndikukutumiza+ 18 kuti ukatsegule maso awo,+ kuwachotsa mumdima+ nʼkuwapititsa kowala+ ndiponso kuwachotsa mʼmanja mwa Satana+ nʼkuwapititsa kwa Mulungu. Ukachite zimenezi kuti machimo awo akhululukidwe+ nʼkulandira cholowa pamodzi ndi oyeretsedwa chifukwa chondikhulupirira.’

19 Choncho, Mfumu Agiripa, ine ndinaona kuti ndimvere zimene ndinaona mʼmasomphenya akumwambawo. 20 Kuyambira kwa anthu a ku Damasiko,+ kenako a ku Yerusalemu+ ndipo kenako mʼdziko lonse la Yudeya ndi anthu a mitundu ina, ndinafikitsa uthenga wakuti alape nʼkuyamba kulambira Mulungu pochita zinthu zosonyeza kulapa.+ 21 Nʼchifukwa chake Ayuda anandigwira mʼkachisi nʼkumafuna kundipha.+ 22 Komabe, popeza ndinaona Mulungu akundithandiza, ndikuchitirabe umboni kwa anthu otchuka ndiponso anthu wamba mpaka lero. Sindikunena chilichonse, koma zokhazo zimene aneneri ndi Mose ananena kuti zichitika.+ 23 Zoti Khristu adzavutika,+ ndipo monga woyamba kuukitsidwa,+ adzalalikira kwa anthu awa ndiponso kwa anthu a mitundu ina zokhudza kuwala.”+

24 Pamene Paulo ankanena zimenezi podziteteza, Fesito ananena mokweza mawu kuti: “Wachita misala iwe Paulo! Kuphunzira kwambiri kwakupengetsa!” 25 Koma Paulo anati: “Wolemekezeka a Fesito, inetu sindinachite misala, koma ndikulankhula mawu a choonadi ndipo ndili bwinobwino. 26 Kunena zoona, ndikulankhula momasuka chifukwa mfumu imene ndikulankhula nayo ikudziwa bwino zimenezi. Sindikukayikira kuti palibe ngakhale chimodzi mwa zinthu zimenezi, chimene simukuchidziwa chifukwa zimenezi sizinachitike mwamseri.+ 27 Kodi inuyo, Mfumu Agiripa, mumakhulupirira zimene aneneri analemba? Ndikudziwa kuti mumazikhulupirira.” 28 Koma Agiripa anauza Paulo kuti: “Pa nthawi yochepa ukhoza kundikopa kuti ndikhale Mkhristu.” 29 Ndiyeno Paulo anati: “Kaya pa nthawi yochepa kapena yaitali, pemphero langa kwa Mulungu ndi lakuti, onse amene andimvetsera lero, osati inu nokha, akhale ngati ine kupatulapo maunyolo okhawa.”

30 Kenako mfumu inaimirira. Bwanamkubwa, Berenike ndiponso amuna amene anakhala nawo pamodzi nawonso anaimirira. 31 Koma pochoka anayamba kukambirana kuti: “Munthu uyu sanachite chilichonse choyenera kuphedwa kapena kumangidwa.”+ 32 Ndipo Agiripa anauza Fesito kuti: “Akanakhala kuti sanapemphe kukaonekera kwa Kaisara, munthu ameneyu akanamasulidwa.”+

27 Ulendo wathu wapamadzi wopita ku Italy+ utatsimikizika, Paulo ndi akaidi ena anaperekedwa mʼmanja mwa mtsogoleri wa asilikali dzina lake Yuliyo, wamʼgulu la asilikali la Augusito. 2 Ku Adiramutiyo tinakwera ngalawa imene inali itatsala pangʼono kunyamuka ulendo wopita kumadoko amʼmbali mwa nyanja mʼchigawo cha Asia. Kenako tinanyamuka limodzi ndi Arisitako,+ yemwe anali wa ku Makedoniya ku Tesalonika. 3 Tsiku lotsatira tinafika ku Sidoni, ndipo Yuliyo anakomera mtima Paulo moti anamulola kupita kwa anzake kuti akamusamalire.

4 Titalowanso panyanja kuchokera kumeneko, tinayenda mʼmbali mwa chilumba cha Kupuro chimene chinkatiteteza ku mphepo imene inkawomba kuchokera kumene ife tinkapita. 5 Tinayenda panyanja molambalala Kilikiya ndi Pamfuliya ndipo tinafika padoko la Mura, ku Lukiya. 6 Kumeneko mtsogoleri wa asilikali anapeza ngalawa yochokera ku Alekizandiriya yomwe inkapita ku Italy ndipo anatikweza mmenemo. 7 Choncho tinayenda pangʼonopangʼono kwa masiku angapo ndipo tinafika ku Kinido movutikira. Chifukwa cha mphepo yomwe inkawomba kuchokera kutsogolo kwathu, tinadzera ku Salimone kuti chilumba cha Kerete chizititeteza ku mphepoyo. 8 Titayenda movutikira mʼmbali mwa chilumba chimenechi, tinafika pamalo ena otchedwa Madoko Okoma, amene anali pafupi ndi mzinda wa Laseya.

9 Tsopano panali patapita nthawi yaitali, ndipo kuyenda panyanja kunali koopsa chifukwa ngakhale nthawi ya kusala kudya kwa Tsiku la Mwambo Wophimba Machimo+ inali itadutsa kale. Choncho Paulo anawapatsa malangizo. 10 Iye anawauza kuti: “Anthu inu, ndikuona kuti ulendowu tikauyamba panopa tiwonongetsa zambiri. Tiwonongetsa katundu ndiponso ngalawa, ngakhalenso miyoyo yathu.” 11 Koma mtsogoleri wa asilikali anamvera woyendetsa ngalawa ndi mwiniwake wa ngalawayo mʼmalo momvera zimene Paulo ananena. 12 Popeza dokolo silinali labwino kukhalapo nthawi yozizira, anthu ambiri anagwirizana ndi zoti achokepo. Iwo ankafuna kuona ngati nʼzotheka kukafika ku Finikesi kuti akakhale kumeneko nthawi yozizira. Finikesi linali doko la Kerete loyangʼana kumpoto chakumʼmawa ndi kumʼmwera chakumʼmawa.

13 Mphepo yakumʼmwera itayamba kuwomba pangʼonopangʼono, anaganiza kuti zimene ankafuna zitheka. Choncho anakweza nangula nʼkuyamba kuyenda mʼmbali mwa chilumba cha Kerete. 14 Koma pasanapite nthawi, mphepo yamkuntho yotchedwa Yulakilo* inayamba kuwomba ngalawayo. 15 Popeza ngalawa inkawombedwa ndi mphepo yamphamvu ndipo sitinathe kuiwongolera kuti iyende moyangʼana kumene mphepoyo inkachokera, tinagonja ndipo tinatengedwa nayo. 16 Kenako tinayamba kuyenda mʼmbali mwa chilumba china chachingʼono chotchedwa Kauda chimene chinkatiteteza ku mphepo. Komabe tinkalephera kuwongolera bwato lalingʼono limene ngalawayo inkakoka. 17 Ndiyeno atakweza bwatolo mʼngalawa, anayamba kumanga ngalawayo ndi zomangira kuti ilimbe. Ndipo poopa kuti ngalawayo ingatitimire mumchenga ku Suriti,* iwo anatsitsa zingwe zomangira chinsalu cha ngalawa moti inkakankhidwa ndi mphepo. 18 Koma popeza mphepo yamkuntho inkatiwomba ndiponso kutikankha mwamphamvu, tsiku lotsatira anthu anayamba kutaya katundu kuti ngalawa ipepukidwe. 19 Tsiku lachitatu, anataya zingwe zokwezera chinsalu cha ngalawayo.

20 Titaona kuti dzuwa komanso nyenyezi sizinaoneke kwa masiku ambiri komanso tikukankhidwa ndi chimphepo champhamvu, tinayamba kukayikira zoti tipulumuka. 21 Anthuwo atakhala nthawi yaitali osadya kanthu, Paulo anaima pakati pawo nʼkunena kuti: “Anthu inu, mukanamvera malangizo anga, osachoka ku Kerete kuja, sitikanavutika chonchi komanso katundu sakanawonongeka.+ 22 Komabe musadandaule chifukwa palibe amene ataye moyo wake, koma ngalawa yokhayi iwonongeka. 23 Usiku wapitawu mngelo+ wa Mulungu wanga amene ndikumuchitira utumiki wopatulika, anaima pafupi ndi ine 24 nʼkunena kuti: ‘Usaope Paulo. Uyenera kukaima pamaso pa Kaisara.+ Ndipo dziwa kuti chifukwa cha iwe, Mulungu apulumutsa anthu onse amene uli nawo pa ulendowu.’ 25 Choncho limbani mtima anthu inu, chifukwa ndikukhulupirira kuti Mulungu achita zonse zimene wandiuza. 26 Komabe, ngalawa yathuyi iwonongeka pafupi ndi chilumba chinachake.”+

27 Pa usiku wa 14, mphepo inayamba kutikankhira uku ndi uku panyanja ya Adiriya. Ndiyeno pakati pa usiku, oyendetsa ngalawayo anayamba kuganiza kuti akuyandikira kumtunda. 28 Choncho anayeza kuzama kwa nyanja nʼkupeza kuti inali mamita 36. Atayenda kamtunda pangʼono anayezanso kuzama kwake nʼkupeza mamita 27. 29 Koma poopa kuti tiwomba miyala, anatsitsa anangula 4 kumbuyo kwa ngalawayo ndipo ankalakalaka kutangocha. 30 Tsopano oyendetsa ngalawayo ankafuna kuthawamo. Choncho anatsitsira bwato lija panyanja ponamizira kuti akufuna kutsitsa anangula kutsogolo kwa ngalawayo. 31 Paulo anauza mtsogoleri wa asilikali ndi asilikaliwo kuti: “Anthu awa akachoka mʼngalawa muno, simupulumuka.”+ 32 Kenako asilikaliwo anadula zingwe za bwatolo nʼkulisiya kuti lipite.

33 Kutatsala pangʼono kucha, Paulo anayamba kuuza onse kuti adye. Iye anati: “Tsopano patha masiku 14 mukudikirira komanso muli ndi nkhawa ndipo simunadye chilichonse. 34 Choncho ndikukulimbikitsani kuti mudye kuti zinthu zikuyendereni bwino. Chifukwa ngakhale tsitsi limodzi lamʼmutu mwanu siliwonongeka.” 35 Atanena zimenezi, anatenga mkate. Kenako anayamika Mulungu pamaso pa onse nʼkugawagawa mkatewo ndipo iye anayamba kudya. 36 Atatero, onse analimba mtima nʼkuyamba kudya. 37 Tonse pamodzi, mʼngalawamo tinalimo anthu 276. 38 Onse atadya nʼkukhuta, anatayira tirigu mʼnyanja kuti ngalawayo ipepukidwe.+

39 Kutacha, sanadziwe kuti ali kuti,+ koma anaona gombe linalake lamchenga ndipo ankafunitsitsa kuti ngati nʼkotheka akaimitse ngalawa pamenepo. 40 Choncho anadula zingwe za anangula nʼkuzigwetsera mʼnyanja. Anamasulanso zingwe zomangira nkhafi zowongolera. Atakweza mʼmwamba nsalu yakutsogolo ya ngalawa, anayamba kulowera kugombelo. 41 Kenako anafika pachimulu cha mchenga chomwe mafunde ankachiwomba mbali zonse. Kutsogolo kwa ngalawayo kunakanirira pansi mumchengawo osasunthika ndipo mafunde amphamvu anayamba kuwomba kumbuyo kwake moti inayamba kusweka zidutswazidutswa. 42 Zitatero asilikali anaganiza zopha akaidi kuti pasapezeke aliyense wosambira nʼkuthawa.+ 43 Koma mtsogoleri wa asilikali ankafunitsitsa kuti Paulo akafike naye ali bwinobwino, choncho anawaletsa kuchita zimene ankafunazo. Ndiyeno analamula odziwa kusambira kuti alumphire mʼnyanjamo kuti akhale oyamba kukafika kumtunda. 44 Analamulanso ena onse kuti achite chimodzimodzi, ena pamatabwa ndipo ena pa zidutswa za ngalawayo. Pamapeto pake onse anafika kumtunda ali bwinobwino.+

28 Titapulumuka choncho, tinamva kuti chilumbacho chimatchedwa Melita.+ 2 Anthu olankhula chilankhulo chachilendo kumeneko anatisonyeza kukoma mtima kwapadera. Iwo anasonkha moto nʼkutilandira bwino tonse chifukwa kunkagwa mvula ndiponso kunkazizira. 3 Koma Paulo atatola nkhuni nʼkuziponya pamoto, panatuluka njoka ya mphiri chifukwa cha kutentha ndipo inamuluma nʼkukanirira kudzanja lake. 4 Anthu achilankhulo chachilendowo ataona njoka yapoizoni ikulendewera kudzanja lake, anayamba kuuzana kuti: “Ndithu munthu uyu ndi wopha anthu chifukwa ngakhale kuti wapulumuka panyanja, Chilungamo* sichinamulole kuti akhalebe ndi moyo.” 5 Koma iye anakutumulira njokayo pamoto ndipo sinamuvulaze. 6 Anthuwo ankayembekezera kuti atupa kapena agwa mwadzidzidzi nʼkufa. Koma atayembekezera kwa nthawi yaitali nʼkuona kuti palibe chimene chikumuchitikira, anasintha maganizo nʼkuyamba kunena kuti ndi mulungu.

7 Pafupi ndi malowa, panali minda ya munthu woyangʼanira chilumbacho, dzina lake Papuliyo. Iyeyu anatilandira bwino kwambiri ndipo anatichereza kwa masiku atatu. 8 Koma bambo ake a Papuliyo ankadwala malungo* komanso kamwazi ndipo anali chigonere. Choncho Paulo analowa mmene bambowo anali nʼkupemphera ndipo kenako anawagwira pamutu* nʼkuwachiritsa.+ 9 Zitatero, anthu ena onse amene ankadwala pachilumbacho, anabwera kwa iye ndipo anawachiritsa.+ 10 Iwo anatilemekeza potipatsa mphatso zambiri, komanso pamene tinkanyamuka anatipatsa zinthu zambiri zimene tinkafunikira.

11 Patapita miyezi itatu, tinanyamuka pangalawa ya ku Alekizandiriya yokhala ndi chizindikiro cha “Ana a Zeu.” Ngalawa imeneyi inaima pachilumbapo poyembekezera kuti nyengo yozizira ithe. 12 Kenako tinafika padoko lina ku Surakusa ndipo tinakhalapo masiku atatu. 13 Titachoka kumeneko, tinazungulira nʼkukafika ku Regio. Patatha tsiku limodzi, kunayamba kuwomba mphepo yakumʼmwera ndipo tsiku lachiwiri tinafika ku Potiyolo. 14 Kumeneko tinapeza abale ndipo anatipempha kuti tikhale nawo masiku 7. Kenako tinapitiriza ulendo wathu wopita ku Roma. 15 Abale akumeneko atamva za ife, anabwera mpaka kudzafika ku Msika wa Apiyo ndi ku Nyumba Zitatu za Alendo kudzatichingamira. Paulo atawaona, anathokoza Mulungu ndipo analimba mtima.+ 16 Titafika ku Roma, Paulo analoledwa kumakhala yekha ndi msilikali womulondera.

17 Patatha masiku atatu, Paulo anaitanitsa akuluakulu a Ayuda. Atasonkhana, anawauza kuti: “Amuna inu, abale anga, ngakhale kuti sindinachite chilichonse chotsutsana ndi anthu kapena mwambo wa makolo athu,+ anandigwira ku Yerusalemu nʼkundipereka mʼmanja mwa Aroma ngati mkaidi.+ 18 Ndipo atafufuza,+ ankafuna kundimasula chifukwa sanandipeze ndi mlandu woyenera chilango cha imfa.+ 19 Koma Ayuda anatsutsa zimenezo moti ndinakakamizika kupempha kudzaonekera kwa Kaisara.+ Komatu sikuti ndinachita zimenezi chifukwa choti ndinkafuna kudzaneneza mtundu wanga. 20 Pa chifukwa chimenechi, ndinapempha kuti ndidzaonane nanu nʼkulankhula nanu, popeza ndamangidwa ndi unyolo uwu chifukwa cha chiyembekezo cha Aisiraeli.”+ 21 Iwo anamuyankha kuti: “Ife sitinalandire makalata alionse ochokera ku Yudeya onena za iwe. Palibenso aliyense wa abale amene afika kuno, amene watiuza kapena kulankhula choipa chilichonse chokhudza iwe. 22 Komabe tikufuna kumva maganizo ako, chifukwa kunena zoona, ife tonse timadziwa kuti gulu lampatuko limeneli+ amalinenera zoipa kwina kulikonse.”+

23 Zitatero anapangana tsiku loti adzakumane naye ndipo anabweradi ambiri kumene iye ankakhala. Choncho kuyambira mʼmawa mpaka madzulo, anawafotokozera nkhani yonse ndipo anachitira umboni mokwanira za Ufumu wa Mulungu. Anachita zimenezi pogwiritsa ntchito mfundo zokopa zokhudza Yesu,+ kuchokera mʼChilamulo cha Mose+ ndi zimene aneneri analemba.+ 24 Ena anayamba kukhulupirira zimene Paulo ananenazo, koma ena sanakhulupirire. 25 Choncho, popeza ankatsutsana, anayamba kuchoka. Koma Paulo ananena mawu awa:

“Mzimu woyera unanena zoona kwa makolo anu kudzera mwa Yesaya mneneri. 26 Mzimuwo unati, ‘Pita ukauze anthu awa kuti: “Kumva mudzamva ndithu, koma simudzazindikira. Kuyangʼana mudzayangʼana ndithu, koma simudzaona chilichonse.+ 27 Chifukwa anthu awa aumitsa mitima yawo ndipo amva ndi makutu awo, koma osalabadira. Atseka maso awo kuti asaone ndi maso awo komanso kuti asamve ndi makutu awo nʼkumvetsa tanthauzo lake mʼmitima yawo, kenako nʼkutembenuka kuti ine ndiwachiritse.”’+ 28 Choncho dziwani kuti njira ya Mulungu yopulumutsira anthu, yatumizidwa kwa anthu a mitundu ina.+ Ndipo mosakayikira, iwo adzamvetsera.”+ 29*⁠——

30 Choncho Paulo anakhalabe kwa zaka ziwiri zathunthu mʼnyumba yomwe ankapanga lendi,+ ndipo anthu onse omwe ankabwera kudzamuona ankawalandira ndi manja awiri. 31 Ankawalalikira za Ufumu wa Mulungu komanso kuwaphunzitsa za Ambuye Yesu Khristu, ndi ufulu wonse wa kulankhula*+ popanda choletsa.

Kapena kuti, “kumadera akutali.”

Ulendo umenewu unali wautali pafupifupi kilomita imodzi.

Onani Zakumapeto A5.

Kapena kuti, “ankaonedwa ngati atumwi ena 11 aja.”

Kapena kuti, “kulankhula malilime.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “ola lachitatu,” kuwerenga kuchokera 6 koloko mʼmawa.

Kapena kuti, “ndidzatsanulira.”

Onani Zakumapeto A5.

Onani Zakumapeto A5.

Mabaibulo ena amati, “zingwe.”

Onani Zakumapeto A5.

Kapena kuti, “simudzasiya moyo wanga.”

Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Kapena kuti, “liwole.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “ndikakhala pafupi ndi nkhope yanu.”

Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Kapena kuti, “watitsanulira.”

Onani Zakumapeto A5.

Onani Zakumapeto A5.

Kapena kuti, “kugawana zinthu.”

Onani Zakumapeto A5.

Mʼchilankhulo choyambirira, “ola la 9,” kuwerenga kuchokera 6 koloko mʼmawa.

Kutanthauza timafupa tomwe timalumikiza phazi ndi mwendo.

Mʼchilankhulo choyambirira, “kuchokera pankhope ya Yehova.” Onani Zakumapeto A5.

Onani Zakumapeto A5.

Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”

Sankatanthauza osadziwa kulemba ndi kuwerenga, koma osapita kusukulu za Arabi.

Mʼchilankhulo choyambirira, “Sanihedirini.”

Kapena kuti, “ikusinkhasinkha.”

Onani Zakumapeto A5.

Kapena kuti, “Khristu.”

Onani Zakumapeto A5.

Mʼchilankhulo choyambirira, “anali ndi mtima umodzi ndi maganizo amodzi.”

Onani Zakumapeto A5.

Onani Zakumapeto A5.

Kapena kuti, “anangowamenya.”

Kapena kuti, “anawaika manja.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”

Mabaibulo ena amati, “Isaki anachitanso chimodzimodzi ndi.”

Kapena kuti, “zokayendera.”

Onani Zakumapeto A5.

Onani Zakumapeto A5.

Onani Zakumapeto A5.

Onani Zakumapeto A5.

Kapena kuti, “anagona tulo ta imfa.”

Kapena kuti, “kuwaika manja anthuwo.”

Kapena kuti, “ndingamuike manja.”

Onani Zakumapeto A5.

Mʼchilankhulo choyambirira, “ndulu yowawa.”

Onani Zakumapeto A5.

Onani Zakumapeto A5.

Onani Zakumapeto A5.

Onani Zakumapeto A3.

Onani Zakumapeto A5.

Mawu akuti “Njirayo” akutanthauza moyo wa Chikhristu komanso zimene Akhristu amakhulupirira.

Kapena kuti, “nʼkumuika manja.”

Kapena kuti, “anamuika manja.”

Onani Zakumapeto A5.

Dzina loti “Dorika” ndi la Chigiriki ndipo “Tabita” ndi la Chiaramu. Mayina onsewa amatanthauza “Mbawala.”

Ankayangʼanira asilikali 100.

Gulu la asilikali a Chiroma omwe ankakhalapo 600.

Mʼchilankhulo choyambirira, “ola la 9,” kuwerenga kuchokera 6 koloko mʼmawa.

Mʼchilankhulo choyambirira, “ola la 6,” kuwerenga kuchokera 6 koloko mʼmawa.

Mʼchilankhulo choyambirira, “ola la 9,” kuwerenga kuchokera 6 koloko mʼmawa.

Onani Zakumapeto A5.

Kapena kuti, “malilime.”

Kapena kuti, “anangoti kukamwa yasaa.”

Onani Zakumapeto A5.

Ameneyu anali Herode Agiripa Woyamba.

Onani Zakumapeto A5.

Onani Zakumapeto A5.

Onani Zakumapeto A5.

Kapena kuti, “Herode ankafuna kumenyana ndi.”

Kapena kuti, “ankayangʼanira chipinda chogona cha mfumu.”

Onani Zakumapeto A5.

Onani Zakumapeto A5.

Onani Zakumapeto A5.

Kapena kuti, “anawaika manja.”

Kapena kuti, “ankawathandiza.”

Onani Zakumapeto A5.

Onani Zakumapeto A5.

Ena amati “chifunga.”

Onani Zakumapeto A5.

Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”

Kapena kuti, “mʼmanda achikumbutso.”

Kapena kuti, “limawola.”

Onani Zakumapeto A5.

Onani Zakumapeto A5.

Onani Zakumapeto A5.

Onani Zakumapeto A5.

Onani Zakumapeto A5.

Onani Zakumapeto A5.

Kapena kuti, “msasa; nyumba.”

Onani Zakumapeto A5.

Onani Zakumapeto A5.

Kapena kuti, “maganizo.”

MʼChigiriki por·nei′a. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Kapena kuti, “nyama imene yaphedwa osazinga kuti magazi atuluke.” Ena amati kusinga.

Kapena kuti, “nyama imene yaphedwa osazinga kuti magazi atuluke.” Ena amati kusinga.

MʼChigiriki por·nei′a. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Kapena kuti, “moyo wathanzi.”

Onani Zakumapeto A3.

Onani Zakumapeto A5.

Onani Zakumapeto A5.

Onani Zakumapeto A5.

Onani Zakumapeto A5.

Onani Zakumapeto A5.

Onani Zakumapeto A5.

Kapena kuti, “ndalama za belo.”

Kapena kuti, “ndinu opembedza kwambiri.”

Kapena kuti, “mbadwa zake.”

Kutanthauza kusunagoge.

Bwanamkubwa wachigawo cha Roma. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Onani Zakumapeto A5.

Zikuoneka kuti anapita ku Yerusalemu.

Kapena kuti, “analangizidwa ndi mawu apakamwa.”

Onani Zakumapeto A5.

Kapena kuti, “atawaika manja.”

Kapena kuti, “zilankhulo zosiyanasiyana.”

Kapena kuti, “maepuloni.”

Onani Zakumapeto A5.

Bwanamkubwa wachigawo cha Roma. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Mʼchilankhulo choyambirira, “ananyemanyema mkate ndipo anayamba kudya.”

Kapena kuti, “wamtengo wapatali.”

Kapena kuti, “zonse zimene Mulungu akufuna kuchita.”

Kapena kuti, “anamukumbatira.”

Kapena kuti, “mbali imene kunali doko.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “omwe anali anamwali.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “tinakhala chete.”

Onani Zakumapeto A5.

Kapena kuti, “nyama imene yaphedwa osazinga kuti magazi atuluke.” Ena amati kusinga.

MʼChigiriki por·nei′a. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Ena amati, “kumukuwa kapena kumuwowoza.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “ola lachitatu,” kuwerenga kuchokera 6 koloko madzulo.

Ena amati “mahosi.”

Kapena kuti, “loya wina.”

Onani Zakumapeto A3.

Kapena kuti, “zokhudza chipembedzo chawo.”

Zimenezi zinali ndodo zosongola zimene ankatosera nyama zapagoli kuti ziziyenda mofulumira.

Imeneyi ndi mphepo yochokera kumpoto chakumʼmawa.

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

MʼChigiriki Di′ke. Mawuwa mwina akunena za mulungu wamkazi wobwezera kuti chilungamo chioneke. Kapenanso anangowagwiritsa ntchito potanthauza chilungamo.

Mʼchilankhulo choyambirira, “anatentha thupi.”

Kapena kuti, “anawaika manja.”

Onani Zakumapeto A3.

Kapena kuti, “molimba mtima kwambiri.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena