Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • nwt Exodus 1:1-40:38
  • Ekisodo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ekisodo
  • Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Ekisodo

EKISODO

1 Ndiyeno awa ndi mayina a ana a Isiraeli kapena kuti Yakobo, amene anapita nawo ku Iguputo. Mwana wamwamuna aliyense anapita limodzi ndi banja lake:+ 2 Rubeni, Simiyoni, Levi, Yuda,+ 3 Isakara, Zebuloni, Benjamini, 4 Dani, Nafitali, Gadi ndi Aseri.+ 5 Ana onse a Yakobo komanso zidzukulu zake* analipo 70, koma Yosefe anali kale ku Iguputo.+ 6 Patapita nthawi Yosefe anamwalira,+ chimodzimodzinso abale ake onse ndi anthu a mʼbadwo wonsewo. 7 Aisiraeli* anaberekana ndipo anachuluka kwambiri mʼdzikomo. Iwo anapitiriza kukhala amphamvu komanso anachulukana mofulumira kwambiri, moti anadzaza mʼdzikomo.+

8 Patapita nthawi, mfumu ina yomwe sinkamudziwa Yosefe inayamba kulamulira ku Iguputo. 9 Mfumuyo inauza anthu ake kuti: “Taonani! Aisiraeli achuluka kwambiri ndipo ndi amphamvu kuposa ife.+ 10 Tiyeni tiwachenjerere anthu amenewa kuti asapitirize kuchulukana, kuopera kuti pa nthawi ya nkhondo angadzagwirizane ndi adani athu nʼkumenyana nafe kenako nʼkuchoka mʼdziko muno.”

11 Choncho anaika akapitawo oti aziwayangʼanira pa ntchito yawo yaukapolo kuti aziwazunza powagwiritsa ntchito mwankhanza.+ Ndipo anamangira Farao mizinda ya Pitomu ndi Ramese+ kuti ikhale mosungiramo zinthu.* 12 Koma pamene ankawazunza kwambiri mʼpamenenso ankawonjezeka komanso kufalikira kwambiri, moti Aiguputo anachita mantha kwambiri chifukwa cha Aisiraeliwo.+ 13 Choncho Aiguputo anakakamiza Aisiraeli kuti azigwira ntchito yaukapolo mwankhanza.+ 14 Iwo anasautsa moyo wa Aisiraeliwo powagwiritsa ntchito yowawa, yomwe inali yoponda matope ndi kuumba njerwa. Anawagwiritsa ntchito yaukapolo wa mtundu uliwonse mʼmunda. Ankawazunza komanso kuwagwiritsa ntchito ya mtundu uliwonse wa ukapolo.+

15 Kenako mfumu ya Iguputo inalankhula ndi azamba* a Chiheberi, amene mayina awo anali Sifira ndi Puwa. 16 Iye anawauza kuti: “Mukamathandiza amayi a Chiheberi kubereka+ ndipo mwaona kuti mwana amene akubadwayo ndi wamwamuna muzimupha, koma ngati ndi wamkazi muzimusiya wamoyo.” 17 Koma azambawo ankaopa Mulungu woona, ndipo sanachite zimene mfumu ya Iguputo inawauza. Mʼmalomwake, ana aamuna ankawasiya amoyo.+ 18 Patapita nthawi, mfumu ya Iguputo inaitana azamba aja nʼkuwafunsa kuti: “Nʼchifukwa chiyani ana aamuna mwakhala mukuwasiya amoyo?” 19 Azambawo anauza Farao kuti: “Akazi a Chiheberi sali ngati akazi a ku Iguputo kuno. Akazi a Chiheberi ndi amphamvu, moti mzamba asanafike iwo amakhala atabereka kale.”

20 Choncho Mulungu anawadalitsa azambawo, ndipo Aisiraeli anapitiriza kuwonjezeka nʼkukhala amphamvu kwambiri. 21 Chifukwa chakuti azambawo anaopa Mulungu woona, patapita nthawi iye anawadalitsa powapatsa ana awoawo. 22 Kenako Farao analamula anthu ake onse kuti: “Mwana aliyense wamwamuna wobadwa kumene wa Aheberi muzimuponya mumtsinje wa Nailo, koma mwana aliyense wamkazi muzimusiya wamoyo.”+

2 Pa nthawiyo, mwamuna wina wa fuko la Levi anakwatira mkazi amene analinso wa fuko la Levi.+ 2 Mkaziyo anakhala woyembekezera nʼkubereka mwana wamwamuna. Ataona kuti mwanayo ndi wokongola, anamubisa kwa miyezi itatu.+ 3 Mwanayo atafika poti sangathenso kumubisa,+ anatenga kabasiketi* kagumbwa* nʼkukamata phula. Kenako anaikamo mwanayo nʼkukasiya kabasiketiko pakati pa mabango mʼmphepete mwa mtsinje wa Nailo. 4 Koma mchemwali wake+ anaima chapatali kuti aone zimene zingachitikire mwanayo.

5 Mwana wamkazi wa Farao atapita kukasamba mumtsinje wa Nailo, atsikana ake omutumikira ankayenda mʼmphepete mwa mtsinjewo. Kenako iye anaona kabasiketi kaja kali pakati pa mabango. Nthawi yomweyo anatuma kapolo wake wamkazi kuti akakatenge.+ 6 Atakatsegula anaona kuti muli mwana wamwamuna, ndipo ankalira. Iye anamumvera chisoni, koma ananena kuti: “Uyu ndi mmodzi wa ana a Aheberi.” 7 Zitatero, mchemwali wake uja anauza mwana wa Farao kuti: “Kodi mungakonde kuti ndikakuitanireni mayi woyamwitsa wa Chiheberi kuti akulerereni mwanayu?” 8 Mwana wa Faraoyo anamuyankha kuti: “Inde pita!” Nthawi yomweyo mtsikanayo anapita kukaitana mayi ake+ a mwanayo. 9 Ndiyeno mwana wa Farao anauza mayiyo kuti: “Tenga mwanayu ukandilerere ndipo ine ndizikulipira.” Choncho mayiyo anatenga mwanayo ndipo anamulera. 10 Mwana uja atakula, anapita naye kwa mwana wa Farao, ndipo anakhala mwana wake.+ Zitatero anamʼpatsa dzina lakuti Mose* nʼkunena kuti: “Chifukwa chakuti ndinamuvuula mʼmadzi.”+

11 Tsopano mʼmasiku amenewo, Mose atakula* anapita kwa abale ake kuti akaone mmene ankavutikira ndi ntchito yaukapolo+ imene ankagwira. Kumeneko anaona mʼbale wake wa Chiheberi akumenyedwa ndi nzika ina ya ku Iguputo. 12 Choncho anayangʼana uku ndi uku ndipo ataona kuti palibe amene akumuona, anapha munthu wa ku Iguputoyo nʼkumubisa mumchenga.+

13 Koma tsiku lotsatira atapitanso, anapeza amuna awiri a Chiheberi akumenyana. Choncho anafunsa wolakwayo kuti: “Ukumʼmenyeranji mnzako?”+ 14 Poyankha iye anati: “Ndi ndani anakupatsa udindo woti uzitilamulira komanso kutiweruza? Kodi ukufuna kundipha ngati mmene unaphera nzika ya mu Iguputo ija?”+ Zitatero Mose anachita mantha ndipo mumtima mwake anati: “Apa nkhani ija yadziwika basi!”

15 Kenako Farao anamva za nkhaniyi ndipo ankafuna kupha Mose. Koma Mose anathawa Farao nʼkupita kukakhala kudziko la Midiyani.+ Atafika kumeneko, anakhala pafupi ndi chitsime. 16 Ndiyeno wansembe wa ku Midiyani+ anali ndi ana aakazi 7. Iwo anafika pachitsimepo kuti atunge madzi ndi kuwathira momwera ziweto kuti ziweto za bambo awo zimwe. 17 Koma monga mwa masiku onse, kunafika abusa nʼkuthamangitsa atsikanawo. Zitatero Mose ananyamuka nʼkuthandiza* atsikanawo, ndipo iye anamwetsa ziweto zawo. 18 Ndiyeno atsikanawo atafika kunyumba, bambo awo a Reueli*+ anadabwa ndipo anati: “Bwanji mwabwerako mwamsanga chonchi lero?” 19 Iwo anayankha kuti: “Munthu wina wa ku Iguputo+ watilanditsa kwa abusa, komanso watitungira madzi nʼkutimwetsera ziweto.” 20 Iye anafunsa ana akewo kuti: “Nanga iyeyo ali kuti? Mwamusiyiranji? Pitani mukamuitane kuti tidzadye naye chakudya.” 21 Zitatero Mose anavomereza kukhala ndi Reueli, ndipo iye anapereka Zipora+ mwana wake wamkazi kwa Mose kuti akhale mkazi wake. 22 Kenako Zipora anabereka mwana wamwamuna ndipo Mose anamʼpatsa dzina lakuti Gerisomu,*+ chifukwa anati, “Ndakhala mlendo mʼdziko lachilendo.”+

23 Patapita nthawi yaitali mfumu ya Iguputo inamwalira.+ Koma Aisiraeli anapitirizabe kuvutika chifukwa cha ukapolo ndipo ankalira modandaula. Iwo anapitirizabe kulirira Mulungu woona+ kuti awathandize chifukwa cha ukapolowo. 24 Patapita nthawi, Mulungu anamva kubuula+ kwawo ndipo anakumbukira pangano lake ndi Abulahamu, Isaki ndi Yakobo.+ 25 Choncho Mulungu anayangʼana Aisiraeli ndipo anaona mmene ankavutikira.

3 Mose anakhala mʼbusa wa ziweto za Yetero*+ apongozi ake, wansembe wa ku Midiyani. Pamene ankaweta ziwetozo chakumadzulo kwa chipululu, anafika kuphiri la Mulungu woona, ku Horebe.+ 2 Kenako mngelo wa Yehova anaonekera kwa iye pakati pa chitsamba chaminga+ chimene chinkayaka moto. Atachiyangʼanitsitsa, anaona kuti chitsamba chamingacho chikuyaka, koma sichikunyeka. 3 Choncho Mose anati: “Ndipite kuti ndikaonetsetse zodabwitsa zimenezi. Ndikaone chifukwa chake chitsamba chamingachi chikuyaka koma osanyeka.” 4 Yehova ataona kuti Mose wapita kuti akaonetsetse, Mulungu anamuitana kuchokera pachitsamba chamingacho kuti: “Mose! Mose!” ndipo iye anayankha kuti: “Ine mbuyanga.” 5 Ndiyeno Mulungu anati: “Usayandikire kuno. Vula nsapato zako chifukwa malo waimawo ndi malo oyera.”

6 Iye ananenanso kuti: “Ndine Mulungu wa makolo* ako, Mulungu wa Abulahamu,+ Mulungu wa Isaki+ ndi Mulungu wa Yakobo.”+ Atatero Mose anaphimba nkhope yake chifukwa ankaopa kuyangʼana Mulungu woona. 7 Yehova anawonjezera kuti: “Ndaona mmene anthu anga amene ali ku Iguputo akuvutikira, ndipo ndamva kulira kwawo chifukwa cha amene akuwagwiritsa ntchito mwankhanza. Ndikudziwa bwino ululu umene akumva.+ 8 Choncho ndipita kuti ndikawapulumutse mʼmanja mwa Aiguputo+ ndi kuwatulutsa mʼdzikolo nʼkuwalowetsa mʼdziko labwino komanso lalikulu, dziko loyenda mkaka ndi uchi.+ Ndiwalowetsa mʼdziko la Akanani, Ahiti, Aamori, Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi.+ 9 Taona, ndamva kulira kwa Aisiraeli komanso ndaona nkhanza zimene Aiguputo akuwachitira powapondereza.+ 10 Tsopano tamvera, ndikutuma kwa Farao kuti ukatulutse anthu anga Aisiraeli ku Iguputo.”+

11 Koma Mose anayankha Mulungu woona kuti: “Ndine ndani ine kuti ndipite kwa Farao nʼkukatulutsa Aisiraeli ku Iguputo?” 12 Pamenepo Mulungu anati: “Ndidzakhala nawe,+ ndipo chizindikiro chosonyeza kuti ine ndi amene ndakutuma ndi ichi: Pambuyo potulutsa anthuwo mu Iguputo, anthu inu mudzatumikira* Mulungu woona paphiri lino.”+

13 Koma Mose anafunsa Mulungu woona kuti: “Nditati ndapita kwa Aisiraeli nʼkuwauza kuti, ‘Mulungu wa makolo anu wandituma kwa inu,’ iwo nʼkundifunsa kuti, ‘Dzina lake ndi ndani?’+ Ndikawayankhe kuti chiyani?” 14 Mulungu anayankha Mose kuti: “Ndidzakhala Amene Ndidzafune Kukhala.”*+ Ndiyeno anawonjezera kuti: “Aisiraeli ukawauze kuti, ‘Ndidzakhala Amene Ndidzafune Kukhala ndi amene wandituma kwa inu.’”+ 15 Kenako Mulungu anauzanso Mose kuti:

“Aisiraeli ukawauze kuti, ‘Yehova Mulungu wa makolo anu, Mulungu wa Abulahamu,+ Mulungu wa Isaki+ ndi Mulungu wa Yakobo,+ wandituma kwa inu.’ Dzina langa ndi limeneli mpaka kalekale,+ ndipo mibadwo yonse izidzakumbukira dzina limeneli. 16 Ndiye pita ukasonkhanitse akulu a Isiraeli nʼkuwauza kuti, ‘Yehova Mulungu wa makolo anu, Mulungu wa Abulahamu, Isaki ndi Yakobo, anaonekera kwa ine nʼkundiuza kuti: “Ndithu, ndaona zimene zikukuchitikirani+ komanso ndaona zimene akukuchitirani ku Iguputo. 17 Choncho ndikulonjeza kuti, Ndidzakupulumutsani mʼmanja mwa Aiguputo amene akukuzunzani+ nʼkukulowetsani mʼdziko la Akanani, Ahiti, Aamori,+ Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi,+ dziko loyenda mkaka ndi uchi.”’+

18 Iwo adzamvera ndithu mawu ako+ ndipo iweyo ndi akulu a Isiraeli mudzapite kwa mfumu ya Iguputo nʼkukaiuza kuti: ‘Yehova Mulungu wa Aheberi+ walankhula nafe. Ndiye chonde mutilole kuti tiyende ulendo wamasiku atatu kupita mʼchipululu, kuti tikapereke nsembe kwa Yehova Mulungu wathu.’+ 19 Koma ine ndikudziwa bwino kuti mfumu ya Iguputo sidzakulolani kupita, pokhapokha dzanja lamphamvu litaikakamiza kuchita zimenezi.+ 20 Choncho ndidzatambasula dzanja langa nʼkulanga Iguputo ndi ntchito zanga zonse zodabwitsa zimene ndidzachite mʼdzikolo. Ndipo ndikadzachita zimenezi, adzakulolani kuti muchoke.+ 21 Kenako ndidzachititsa kuti Aiguputo akomere mtima anthu anga, moti pochoka simudzachoka chimanjamanja.+ 22 Mkazi aliyense adzapemphe zinthu zasiliva, zagolide ndi zovala kwa munthu wokhala naye pafupi ndi kwa mkazi amene akukhala mʼnyumba mwake. Zinthu zimenezi mudzaveke ana anu aamuna ndi ana anu aakazi, ndipo mudzatenge zinthu zambiri za Aiguputo.”+

4 Koma Mose anayankha kuti: “Bwanji ngati sakandikhulupirira komanso kumvera mawu anga?+ Chifukwatu adzanena kuti, ‘Yehova sanaonekere kwa iwe.’” 2 Kenako Yehova anamufunsa kuti: “Chili mʼdzanja lakocho nʼchiyani?” Mose anayankha kuti: “Ndodo.” 3 Ndiyeno iye anati: “Iponye pansi.” Iye anaiponya pansi ndipo inasanduka njoka.+ Zitatero Mose anayamba kuthawa. 4 Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti: “Igwire kumchira.” Choncho Mose anaigwira ndipo inasandukanso ndodo mʼdzanja lake. 5 Kenako Mulungu anati: “Ukachite zimenezi kuti akakhulupirire kuti Yehova Mulungu wa makolo awo, Mulungu wa Abulahamu, Mulungu wa Isaki ndi Mulungu wa Yakobo,+ anaonekera kwa iwe.”+

6 Yehova anamuuzanso kuti: “Lowetsa dzanja lako mʼmalaya, pachifuwa.” Choncho Mose analowetsa dzanja lake mʼmalaya. Koma atalitulutsa, anaona kuti dzanja lakelo lachita khate ndipo likuoneka loyera kwambiri.+ 7 Ndiyeno Mulungu anati: “Lowetsanso dzanja lako mʼmalayamo.” Choncho analowetsanso dzanja lake mʼmalaya. Atalitulutsa anaona kuti lakhalanso bwino ngati poyamba. 8 Mulungu anamuuza kuti: “Ngati sakakukhulupirira kapena kulabadira chizindikiro choyamba, akakhulupirira chizindikiro chachiwirichi.+ 9 Komabe ngati sakakhulupirira zizindikiro ziwirizi nʼkumvera mawu ako, ukatenge madzi amumtsinje wa Nailo nʼkuwathira panthaka youma. Ndipo madzi amene ukatenge mumtsinje wa Nailowo adzasanduka magazi panthakapo.”+

10 Ndiyeno Mose anauza Yehova kuti: “Pepani Yehova, ine kulankhula kumandivuta kuyambira kalekale. Komanso panopa pamene mukulankhula ndi ine mtumiki wanu, ndikulankhula movutikira* chifukwa ndine wa lilime lolemera.”+ 11 Pamenepo Yehova anamuuza kuti: “Anapatsa munthu pakamwa ndi ndani, kapena ndi ndani amene ali ndi mphamvu zopangitsa munthu kukhala wosalankhula, wogontha, woona kapena wosaona? Kodi si ine, Yehova? 12 Choncho pita, ndipo ukamakalankhula ine ndidzakhala nawe* ndipo ndidzakuuza zoti unene.”+ 13 Koma Mose anati: “Pepani Yehova, chonde, tumizani wina aliyense amene mukufuna kumutumiza.” 14 Zitatero, Yehova anakwiyira kwambiri Mose ndipo anati: “Kodi si paja Aroni+ Mlevi uja ndi mʼbale wako? Ndikudziwa kuti amalankhula bwino kwambiri. Ndiponso, iye ali mʼnjira kudzakuchingamira. Akakuona, adzakondwera kwambiri mumtima mwake.+ 15 Choncho ukalankhule naye ndi kumuuza zoti akanene.+ Ineyo ndidzakhala ndi iwe pamodzi ndi iye mukamakalankhula+ ndipo ndidzakuuzani zochita. 16 Iyeyo ndi amene azikalankhula kwa anthu mʼmalo mwa iwe. Choncho adzakhala wokulankhulira, ndipo iwe udzakhala ngati Mulungu kwa iye.+ 17 Ndodo iyi izikakhala mʼdzanja lako ndipo uzikaigwiritsa ntchito pochita zizindikiro.”+

18 Choncho Mose anapita kwa Yetero apongozi ake+ nʼkuwauza kuti: “Ndikufuna kupita kwa abale anga ku Iguputo kuti ndikaone ngati adakali moyo.” Choncho, Yetero anayankha Mose kuti: “Pita mu mtendere.” 19 Ndiyeno Yehova anamuuza Mose ali ku Midiyani kuti: “Nyamuka, bwerera ku Iguputo, chifukwa onse amene ankafuna kukupha* anafa.”+

20 Kenako Mose anatenga mkazi wake ndi ana ake nʼkuwakweza pabulu, ndipo anayamba ulendo wobwerera ku Iguputo. Komanso Mose anatenga ndodo ya Mulungu woona mʼdzanja lake. 21 Yehova anauzanso Mose kuti: “Ukakafika ku Iguputo ukaonetsetse kuti wachita pamaso pa Farao, zodabwitsa zonse zimene ndakupatsa mphamvu kuti ukachite.+ Koma ine ndidzamulola kuti aumitse mtima wake,+ moti sadzalola anthu anga kuchoka.+ 22 Ukauze Farao kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Isiraeli ndi mwana wanga wamwamuna, mwana wanga woyamba kubadwa.+ 23 Ndikukuuza kuti, Lola mwana wanga apite kuti akanditumikire. Koma ngati ukukana kumulola kuti apite, ndidzapha mwana wako wamwamuna, mwana wako woyamba kubadwa.”’”+

24 Ndiyeno ali pa ulendowo, atafika pamalo oti agone, Yehova+ anakumana naye ndipo ankafuna kumupha.+ 25 Zitatero, Zipora+ anatenga mwala wakuthwa* nʼkumudula mwana wakeyo. Ndipo khungu analidulalo analiponya pansi ndipo linakhudza mapazi ake. Kenako ananena kuti: “Popeza ndinu mkwati wa magazi kwa ine.” 26 Atatero, Mulungu anamusiya. Pamenepo Zipora anati, “mkwati wa magazi,” chifukwa cha mdulidwewo.

27 Kenako Yehova anauza Aroni kuti: “Pita kuchipululu kukachingamira Mose.”+ Choncho Aroni ananyamuka ndipo anakumana ndi Mose paphiri la Mulungu woona,+ ndipo anamulonjera nʼkumukisa.* 28 Atakumana, Mose anauza Aroni mawu onse a Yehova, yemwe anamutuma.+ Anamuuzanso zizindikiro zonse zimene anamulamula kuti achite.+ 29 Kenako Mose ndi Aroni anapita kukasonkhanitsa akulu onse a Aisiraeli.+ 30 Aroni anawauza mawu onse amene Yehova anauza Mose, ndipo Mose anachita zizindikiro+ pamaso pa anthuwo. 31 Zitatero anthuwo anakhulupirira+ Mose. Atamva kuti Yehova akufuna kuthandiza Aisiraeli+ komanso kuti waona mavuto amene akukumana nawo,+ anagwada nʼkuwerama mpaka nkhope zawo pansi.

5 Kenako Mose ndi Aroni anapita kwa Farao nʼkumuuza kuti: “Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Lola anthu anga apite mʼchipululu kuti akachite chikondwerero.’” 2 Koma Farao anati: “Yehova ndi ndani+ kuti ndimvere mawu ake nʼkulola Aisiraeli kuti apite?+ Ine sindikumudziwa Yehova ngakhale pangʼono ndipo sindilola kuti Aisiraeli apite.”+ 3 Komabe iwo anati: “Mulungu wa Aheberi walankhula nafe. Ndiye mutilole chonde, tipite ulendo wamasiku atatu mʼchipululu, kuti tikapereke nsembe kwa Yehova Mulungu wathu.+ Ngati sititero, adzatipha ndi matenda kapena lupanga.” 4 Mfumu ya Iguputo inawayankha kuti: “Nʼchifukwa chiyani iwe Mose ndi Aroni mukufuna kuti anthu asiye ntchito zawo? Bwererani ku ntchito yanu!”*+ 5 Farao anapitiriza kuti: “Anthu amenewa ndi ambiri mʼdziko lino, ndipo inu mukufuna kusokoneza ntchito yawo.”

6 Tsiku lomwelo Farao analamula amene ankawayangʼanira komanso akapitawo awo kuti: 7 “Anthu amenewa musawapatsenso udzu woumbira njerwa.+ Muwasiye azikafuna okha udzu umenewo. 8 Koma muwauze kuti chiwerengero cha njerwa zofunika chikhala chakale chomwe chija. Musawachepetsere chiwerengerocho, chifukwa ayamba ulesi. Nʼchifukwa chake akulira kuti, ‘Tikufuna tipite kukapereka nsembe kwa Mulungu wathu!’ 9 Agwiritseni ntchito yakalavulagaga anthu amenewa ndipo muwapatse ntchito yambiri kuti asamvere zabodza.”

10 Choncho amene ankawayangʼanira+ komanso akapitawo awo anapita kwa Aisiraeliwo nʼkukawauza kuti: “Mverani zimene Farao wanena, ‘Sindikupatsaninso udzu woumbira njerwa. 11 Muzipita nokha kukafuna udzu kulikonse kumene mungaupeze, koma ntchito yanu sichepetsedwa ngakhale pangʼono.’” 12 Chotero, anthu anali balalabalala mʼdziko lonse la Iguputo kukafuna mapesi mʼmalo mwa udzu. 13 Choncho amene ankawayangʼanira aja ankawakakamiza kugwira ntchito ponena kuti: “Aliyense azimaliza ntchito yake tsiku lililonse ngati mmene munkachitira pamene tinkakupatsani udzu.” 14 Kenako oyangʼanira ntchito a Farao anamenya+ akapitawo a Aisiraeli amene iwo anawaika nʼkuwafunsa kuti: “Nʼchifukwa chiyani dzulo ndi lero simunamalize kuumba njerwa zimene munauzidwa ngati mmene munkachitira poyamba?”

15 Zitatero akapitawo a Aisiraeli anapita kwa Farao nʼkukamudandaulira kuti: “Nʼchifukwa chiyani atumiki anu mukuwachitira zimenezi? 16 Ife atumiki anu sitikupatsidwa udzu, koma akutiuza kuti, ‘Umbani njerwa!’ ndipo tikumenyedwa ngakhale kuti olakwa ndi anthu anu.” 17 Koma iye anati: “Mukuchita ulesi, mukuchita ulesi!+ Nʼchifukwa chake mukunena kuti, ‘Tikufuna tipite kukapereka nsembe kwa Yehova.’+ 18 Choncho pitani, kagwireni ntchito! Simuzipatsidwanso udzu, koma chiwerengero cha njerwa zimene muziumba sichisintha.”

19 Pamenepo akapitawo a Aisiraeli anaona kuti zinthu zawaipira kwambiri chifukwa cha zimene anauzidwa kuti: “Musachepetse ngakhale pangʼono chiwerengero cha njerwa zimene aliyense akuyenera kuumba tsiku lililonse.” 20 Zitatero akapitawowa anakumana ndi Mose ndi Aroni, amene ankawadikira kuti aonane nawo pamene amachokera kwa Farao. 21 Nthawi yomweyo iwo anati: “Yehova aone zimene mwachitazi ndipo akuweruzeni chifukwa mwachititsa kuti Farao ndi atumiki ake aipidwe nafe,* moti mwawapatsa lupanga mʼmanja mwawo kuti atiphe.”+ 22 Pamenepo Mose anatembenukira kwa Yehova nʼkunena kuti: “Yehova, nʼchifukwa chiyani mwalola kuti anthuwa azunzike? Nʼchifukwa chiyani munandituma? 23 Kuchokera pamene ndinapita kukalankhula ndi Farao mʼdzina lanu,+ iye wachitira anthu awa zinthu zoipa kwambiri,+ ndipo inu simunapulumutse anthu anu.”+

6 Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti: “Tsopano uona zimene ndichite kwa Farao.+ Dzanja langa lamphamvu limukakamiza kuti awalole kuchoka, ndipo dzanja langa lamphamvu limukakamiza kuti awathamangitse mʼdziko lake.”+

2 Kenako Mulungu anauza Mose kuti: “Ine ndine Yehova. 3 Ndinkaonekera kwa Abulahamu, Isaki ndi Yakobo monga Mulungu Wamphamvuyonse.+ Koma za dzina langa lakuti Yehova,+ ine sindinadzidziwikitse kwa iwo.+ 4 Ndinakhazikitsa pangano langa ndi iwo kuti ndidzawapatsa dziko la Kanani, dziko limene ankakhalamo ngati alendo.+ 5 Tsopano ine ndamva kubuula kwa Aisiraeli, amene Aiguputo akuwagwiritsa ntchito yaukapolo, ndipo ndikukumbukira pangano langa.+

6 Choncho uwauze Aisiraeli kuti, ‘Ine ndine Yehova. Ndidzakupulumutsani ku ntchito yokakamiza imene Aiguputo akukugwiritsani ndipo ndidzakulanditsani kuti musakhalenso akapolo awo.+ Ndidzakuwombolani ndi dzanja langa lotambasula* komanso ndi ziweruzo zamphamvu.+ 7 Choncho ndidzakutengani kuti mukhale anthu anga, ndipo ine ndidzakhala Mulungu wanu.+ Inuyo mudzadziwadi kuti ine ndine Yehova Mulungu wanu, amene ndikukupulumutsani ku ntchito yokakamiza imene Aiguputo akukugwiritsani. 8 Ine ndidzakulowetsani mʼdziko limene ndinalumbira* kuti ndidzalipereka kwa Abulahamu, Isaki ndi Yakobo. Ndidzakupatsani dzikolo kuti likhale lanu.+ Ine ndine Yehova.’”+

9 Kenako Mose anapereka uthenga umenewu kwa Aisiraeli, koma iwo sanamvere Mose chifukwa chokhumudwa ndiponso chifukwa cha ntchito yowawa ya ukapolo.+

10 Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti: 11 “Pita kwa Farao, mfumu ya Iguputo, ukamuuze kuti alole Aisiraeli kutuluka mʼdziko lake.” 12 Koma Mose anayankha Yehova kuti: “Komatu Aisiraeli sanandimvere,+ ndiye Farao akandimvera bwanji? Pajatu ndimalankhula movutikira.”*+ 13 Koma Yehova anauzanso Mose ndi Aroni malamulo oti apereke kwa Aisiraeli ndi kwa Farao, mfumu ya Iguputo, kuti atulutse Aisiraeli mʼdziko la Iguputo.

14 Atsogoleri a mafuko a Aisiraeli ndi awa: Ana aamuna a Rubeni, yemwe anali mwana woyamba kubadwa wa Isiraeli,+ anali Hanoki, Palu, Hezironi ndi Karami.+ Amenewa ndi mabanja a fuko la Rubeni.

15 Ana aamuna a Simiyoni anali Yemueli, Yamini, Ohadi, Yakini, Zohari ndi Shauli, mwana amene anabereka ndi mkazi wa Chikanani.+ Amenewa ndi mabanja a fuko la Simiyoni.

16 Mayina a ana aamuna a Levi,+ mogwirizana ndi mzere wobadwira wa makolo awo ndi awa: Gerisoni, Kohati ndi Merari.+ Ndipo Levi anakhala ndi moyo zaka 137.

17 Ana a Gerisoni anali Libini ndi Simeyi, mogwirizana ndi mabanja awo.+

18 Ndipo ana a Kohati anali Amuramu, Izara, Heburoni ndi Uziyeli.+ Kohati anakhala ndi moyo zaka 133.

19 Ndipo ana aamuna a Merari anali Mali ndi Musi.

Amenewa anali mabanja a Alevi mogwirizana ndi mzere wobadwira wa makolo awo.+

20 Tsopano Amuramu anatenga Yokebedi, mchemwali wa bambo ake, kukhala mkazi wake.+ Ndipo Yokebedi anamʼberekera Amuramu, Aroni ndi Mose.+ Amuramu anakhala ndi moyo zaka 137.

21 Ana aamuna a Izara anali Kora,+ Nefegi ndi Zikiri.

22 Ana aamuna a Uziyeli anali Misayeli, Elizafana+ ndi Sitiri.

23 Aroni anatenga Eliseba, mwana wamkazi wa Aminadabu, mchemwali wake wa Naasoni,+ kukhala mkazi wake. Ndipo Eliseba anamʼberekera Nadabu, Abihu, Eleazara ndi Itamara.+

24 Ana aamuna a Kora anali Asiri, Elikana ndi Abiasafu.+ Amenewa anali mabanja a Kora.+

25 Ndipo Eleazara+ mwana wa Aroni, anatenga mwana wamkazi wa Putieli kukhala mkazi wake. Ndipo iye anamʼberekera Pinihasi.+

Amenewa ndi atsogoleri a mabanja amʼfuko la Levi, mogwirizana ndi mabanja awo.+

26 Umenewu ndi mzere wobadwira wa Aroni ndi Mose, amene Yehova anawauza kuti: “Tulutsani Aisiraeli mʼdziko la Iguputo mʼmagulumagulu.”*+ 27 Anali Mose ndi Aroni+ amene analankhula ndi Farao mfumu ya Iguputo kuti atulutse Aisiraeli mu Iguputo.

28 Pa tsiku limene Yehova analankhula ndi Mose mʼdziko la Iguputo, 29 Yehova anamuuza kuti: “Ine ndine Yehova. Zonse zimene ndikukuuza, ukauze Farao mfumu ya Iguputo.” 30 Ndiye Mose anauza Yehova kuti: “Komatu ndimalankhula movutikira,* ndiye Farao akandimvera bwanji?”+

7 Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti: “Taona, ndakuika kuti ukhale ngati Mulungu* kwa Farao, ndipo Aroni mchimwene wako akhala mneneri wako.+ 2 Iwe uzimuuza zonse zimene ndizikulamula, koma Aroni mchimwene wako ndi amene azikalankhula ndi Farao, ndipo adzaloladi Aisiraeli kuti achoke mʼdziko lake. 3 Koma ine ndidzalola Farao kuti aumitse mtima wake,+ ndipo ndidzachita zizindikiro ndi zodabwitsa zochuluka mʼdziko la Iguputo.+ 4 Komabe Farao sadzakumverani, choncho ndidzaonetsa mphamvu ya dzanja langa pa Iguputo ndi kutulutsa anthu anga Aisiraeli omwe ndi ambiri. Ndidzawatulutsa mʼdziko la Iguputo ndi ziweruzo zamphamvu.+ 5 Pamenepo Aiguputo adzadziwa kuti ine ndine Yehova+ ndikadzatambasula dzanja langa ndi kulanga Iguputo, nʼkutulutsa Aisiraeli mʼdzikolo.” 6 Mose ndi Aroni anachitadi zimene Yehova anawalamula. Anachitadi zomwezo. 7 Pa nthawi imene ankalankhula ndi Farao, Mose anali ndi zaka 80 ndipo Aroni anali ndi zaka 83.+

8 Ndiyeno Yehova anauza Mose ndi Aroni kuti: 9 “Farao akakakuuzani kuti, ‘Chitani chodabwitsa,’ iweyo ukauze Aroni kuti, ‘Tenga ndodo yako nʼkuiponya patsogolo pa Farao.’ Akakachita zimenezo, ikasanduka njoka yaikulu.”+ 10 Choncho Mose ndi Aroni anapita kwa Farao ndipo anachita ndendende mmene Yehova anawalamulira. Aroni anaponya ndodo yake patsogolo pa Farao ndi atumiki ake, ndipo ndodoyo inasanduka njoka yaikulu. 11 Komabe, Farao anaitana amuna anzeru ndi amatsenga ndipo ansembe ochita zamatsenga a ku Iguputo+ nawonso anachita zomwezo mwa matsenga awo.+ 12 Aliyense wa iwo anaponya pansi ndodo yake, ndipo zinasanduka njoka zazikulu. Koma ndodo ya Aroni inameza ndodo zawo. 13 Ngakhale zinali choncho, Farao anaumitsabe mtima wake+ ndipo sanawamvere, mogwirizana ndi zimene Yehova ananena.

14 Kenako Yehova anauza Mose kuti: “Farao waumitsa mtima wake.+ Iye wakana kuti Aisiraeli achoke. 15 Mawa mʼmawa upite kwa Farao. Iye adzakhala akupita kumtsinje. Choncho iweyo udzaime poti udzathe kukumana naye mʼmphepete mwa mtsinje wa Nailo, ndipo udzatenge ndodo imene inasanduka njoka ija.+ 16 Ndiye ukamuuze kuti, ‘Yehova Mulungu wa Aheberi wandituma kwa iwe+ ndi uthenga wakuti: “Lola anthu anga kuchoka kuti akanditumikire mʼchipululu,” koma mpaka pano sukundimvera. 17 Yehova wanena kuti: “Ndimenya madzi amumtsinje wa Nailo ndi ndodo imene ili mʼdzanja langa, ndipo madziwo asanduka magazi. Zikatero udziwa kuti ine ndine Yehova.+ 18 Nsomba zimene zili mumtsinje wa Nailo zifa, ndipo mtsinje wa Nailo ununkha, moti Aiguputo sathanso kumwa madzi ake.”’”

19 Kenako Yehova anauza Mose kuti: “Uza Aroni kuti, ‘Tenga ndodo yako, utambasule dzanja lako nʼkuloza madzi a mu Iguputo.+ Uloze mitsinje yawo, ngalande zawo,* zithaphwi zawo+ ndi malo onse amene amasungira madzi kuti asanduke magazi.’ Choncho madzi amʼdziko lonse la Iguputo, ngakhalenso madzi amʼmitsuko yawo yamtengo ndi yamwala adzakhala magazi.” 20 Nthawi yomweyo Mose ndi Aroni anachita mogwirizana ndi zimene Yehova anawalamula. Aroni anatenga ndodo yake nʼkumenya madzi amumtsinje wa Nailo, Farao ndi atumiki ake akuona ndipo madzi onse amumtsinje wa Nailo anasanduka magazi.+ 21 Zitatero nsomba zamumtsinje wa Nailo zinafa+ ndipo mtsinjewo unayamba kununkha. Aiguputo sanathenso kumwa madzi amumtsinje wa Nailo.+ Mʼdziko lonse la Iguputo munali magazi okhaokha.

22 Koma ansembe ochita zamatsenga a ku Iguputo anachitanso zomwezo mwa matsenga awo,+ moti Farao anapitiriza kuumitsa mtima wake, ndipo sanamvere Mose ndi Aroni, mogwirizana ndi zimene Yehova ananena.+ 23 Kenako Farao anabwerera kunyumba kwake, ndipo sanafune mʼpangʼono pomwe kumvanso za nkhani imeneyi. 24 Choncho Aiguputo onse anayamba kukumba zitsime mʼmphepete mwa mtsinje wa Nailo kuti apeze madzi akumwa, chifukwa sakanatha kumwa madzi a mumtsinje wa Nailo. 25 Ndipo panadutsa masiku 7 kuchokera pamene Yehova anasandutsa madzi amumtsinje wa Nailo kukhala magazi.

8 Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti: “Pita kwa Farao, ukamuuze kuti, ‘Yehova akuti: “Lola anthu anga apite kuti akanditumikire.+ 2 Ukapitiriza kukana kuti apite, ndigwetsa mliri wa achule+ mʼdziko lako lonse. 3 Achulewo adzachuluka kwambiri mumtsinje wa Nailo ndipo adzatuluka mumtsinjemo nʼkulowa mʼnyumba yako, mʼchipinda chako chogona, pabedi pako ndiponso mʼnyumba za atumiki ako, za anthu ako, mʼmauvuni ako ndi mʼziwiya zako zokandiramo ufa.+ 4 Ndipo achulewo adzabwera kwa iwe, anthu ako ndi atumiki ako onse.”’”

5 Kenako Yehova anauza Mose kuti: “Uza Aroni kuti, ‘Tambasula dzanja lako nʼkulozetsa ndodo yako kumitsinje, kungalande zochokera kumtsinje wa Nailo ndi kuzithaphwi, kuti achule atuluke mmenemo nʼkubwera pamtunda mʼdziko lonse la Iguputo.’” 6 Choncho Aroni anatambasula dzanja lake nʼkuloza madzi onse a mu Iguputo, ndipo achule anayamba kutuluka ndi kudzaza dziko lonse la Iguputo. 7 Komabe, ansembe ochita zamatsenga anachitanso zomwezo mwa matsenga awo, ndipo anachititsa achule kubwera pamtunda mʼdziko la Iguputo.+ 8 Kenako Farao anaitana Mose ndi Aroni nʼkuwauza kuti: “Chondererani Yehova kuti achotse achule pa ine ndi anthu anga,+ chifukwa ndikufuna kulola anthu anu kuti apite kukapereka nsembe kwa Yehova.” 9 Ndiyeno Mose anauza Farao kuti: “Munene ndinu kuti ndikachonderere liti kwa Mulungu kuti achulewa achoke kwa inu, kwa atumiki anu, anthu anu ndi mʼnyumba zanu. Achulewa adzangotsala mumtsinje wa Nailo mokha.” 10 Pamenepo Farao anayankha kuti: “Mawa.” Ndiyeno Mose anati: “Zichitika mogwirizana ndi zimene mwanena kuti mudziwe kuti palibenso wina wofanana ndi Yehova Mulungu wathu.+ 11 Achulewa adzachoka kwa inu, mʼnyumba zanu, kwa atumiki anu ndi kwa anthu anu. Adzangotsala mumtsinje wa Nailo mokha.”+

12 Choncho Mose ndi Aroni anachoka pamaso pa Farao, ndipo Mose anachonderera Yehova kuti achotse achule amene Iye anagwetsera Farao.+ 13 Zitatero Yehova anachita mogwirizana ndi zimene Mose anapempha, ndipo achule amene anali mʼnyumba, mʼmabwalo ndi mʼminda anayamba kufa. 14 Aiguputo anayamba kuunjika achulewo mʼmilu yosawerengeka ndipo dziko lonselo linayamba kununkha. 15 Farao ataona kuti mliri wa achulewo watha, anaumitsa mtima wake,+ ndipo sanamvere Mose ndi Aroni, mogwirizana ndi zimene Yehova ananena.

16 Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti: “Uza Aroni kuti, ‘Tenga ndodo yako nʼkumenya fumbi lapansi kuti likhale tizilombo toyamwa magazi* mʼdziko lonse la Iguputo.’” 17 Iwo anachitadi zomwezo. Aroni anatambasula dzanja lake nʼkumenya fumbi lapansi ndi ndodo yake, ndipo tizilomboto tinayamba kusowetsa mtendere anthu ndi nyama zomwe. Fumbi lonse lamʼdziko la Iguputo linasanduka tizilombo toyamwa magazi.+ 18 Ansembe ochita zamatsenga anayesanso kuti apange tizilombo toyamwa magazi pogwiritsa ntchito matsenga awo,+ koma analephera. Ndipo tizilomboto tinkasowetsa mtendere anthu ndi nyama zomwe. 19 Ataona zimenezi ansembe ochita zamatsenga aja anauza Farao kuti: “Chimenechi ndi chala cha Mulungu!”+ Koma Farao anapitiriza kuumitsa mtima wake ndipo sanawamvere, mogwirizana ndi zimene Yehova ananena.

20 Kenako Yehova anauza Mose kuti: “Mawa ulawirire mʼmamawa kwambiri kukakumana ndi Farao akamadzapita kumtsinje, ndipo ukamuuze kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Lola anthu anga apite kuti akanditumikire. 21 Koma ngati sulola kuti anthu anga apite, nditumiza ntchentche zoluma kwa iweyo, atumiki ako, anthu ako ndi mʼnyumba zanu. Ndipo nyumba za mu Iguputo zidzangodzaziratu ndi ntchentche zimenezi komanso pena paliponse pamene pali anthu* moti adzasowa poponda. 22 Pa tsiku limenelo ndidzapatula dera la Goseni kumene kuli anthu anga. Kumeneko sikudzakhala ntchentche zoluma.+ Ndidzachita zimenezi kuti udziwe kuti ine Yehova, ndili mʼdziko lino.+ 23 Ndipo zimene ndidzachitire anthu anga zidzakhala zosiyana ndi zimene ndidzachitire anthu ako. Mawa chizindikiro chimenechi chichitika.”’”

24 Yehova anachitadi zimenezi, moti ntchentche zoluma zinali paliponse mʼnyumba ya Farao, mʼnyumba za atumiki ake ndi mʼdziko lonse la Iguputo.+ Ntchentchezo+ zinabweretsa mavuto aakulu kwa anthu a ku Iguputo. 25 Zitatero, Farao anaitana Mose ndi Aroni nʼkuwauza kuti: “Pitani, kaperekeni nsembe kwa Mulungu wanu koma mʼdziko lomwe lino.” 26 Koma Mose anati: “Sizoyenera kuchita zimenezo, chifukwa nyama zomwe tingapereke nsembe kwa Yehova Mulungu wathu zingakhale zonyansa kwa Aiguputo.+ Kodi Aiguputo sadzatiponya miyala akationa tikupereka nsembe nyama zimene amaziona kuti ndi zonyansa? 27 Ife tipita ulendo wamasiku atatu mʼchipululu, ndipo kumeneko tikapereka nsembe kwa Yehova Mulungu wathu, mogwirizana ndi mmene watiuzira.”+

28 Ndiyeno Farao anati: “Ineyo ndikulolani kuti mupite, ndipo mukaperekadi nsembe kwa Yehova Mulungu wanu mʼchipululu, koma musapite kutali kwambiri. Ndichonderereni kwa Mulungu wanu.”+ 29 Kenako Mose anati: “Ndikachoka pano, ndikupita kukakuchondererani kwa Yehova ndipo mawa ntchentchezi zichoka pa inu Farao, atumiki anu ndi anthu anu. Koma inu Farao musatipusitsenso posalola anthu kupita kuti akapereke nsembe kwa Yehova.”+ 30 Zitatero Mose anachoka kwa Farao nʼkupita kukachonderera Yehova.+ 31 Choncho Yehova anachita mogwirizana ndi zimene Mose anapempha, ndipo ntchentchezo zinachoka kwa Farao, atumiki ake ndi anthu ake. Sipanatsale ntchentche ngakhale imodzi. 32 Koma Farao anaumitsanso mtima wake, ndipo sanalole kuti anthuwo achoke.

9 Choncho Yehova anauza Mose kuti: “Pita kwa Farao, ukamuuze kuti, ‘Yehova Mulungu wa Aheberi wanena kuti: “Lola anthu anga apite kuti akanditumikire.+ 2 Koma ukakana kuti apite nʼkuwaumirirabe, 3 dziwa kuti dzanja la Yehova+ lipha ziweto zanu zonse. Mliri waukulu kwambiri+ ugwera mahatchi,* abulu, ngamila, ngʼombe ndi nkhosa. 4 Ndipo Yehova adzaika malire pakati pa ziweto za Isiraeli ndi ziweto za Iguputo, moti palibe chiweto cha Aisiraeli chimene chidzafe.”’”+ 5 Komanso, Yehova anatchuliratu nthawi kuti: “Mawa, Yehova adzachita zimenezi mʼdzikoli.”

6 Yehova anachitadi zimenezi tsiku lotsatira, moti ziweto zamitundu yonse za Aiguputo zinayamba kufa,+ koma palibe chiweto ngakhale chimodzi cha Aisiraeli chimene chinafa. 7 Ndiye Farao atafufuza anapeza kuti palibe chiweto ngakhale chimodzi cha Aisiraeli chimene chinafa. Ngakhale zinali choncho, Farao anapitiriza kuumitsa mtima wake ndipo sanalole kuti Aisiraeli apite.+

8 Kenako Yehova anauza Mose ndi Aroni kuti: “Tengani phulusa* la mu uvuni lodzaza manja anu awiri ndipo Mose aliponye mʼmwamba Farao akuona. 9 Ndipo lidzachuluka nʼkugwa ngati fumbi padziko lonse la Iguputo. Likatero lidzayambitsa zithupsa pa anthu ndi nyama zomwe, mʼdziko lonse la Iguputo.”

10 Choncho iwo anatenga phulusa la mu uvuni nʼkuima pamaso pa Farao. Kenako Mose analiponya mʼmwamba ndipo linayambitsa zithupsa zimene zinkaphulika pa anthu ndi nyama. 11 Ansembe ochita zamatsenga aja sanathe kuonekera pamaso pa Mose chifukwa cha zithupsazo, popeza zinatuluka pa ansembewo ndi pa Aiguputo onse.+ 12 Koma Yehova analola Farao kuumitsa mtima wake, ndipo sanamvere Mose ndi Aroni, mogwirizana ndi zimene Yehova anauza Mose.+

13 Kenako Yehova anauza Mose kuti: “Mawa ulawirire mʼmamawa kwambiri kukaonana ndi Farao, ndipo ukamuuze kuti: ‘Yehova Mulungu wa Aheberi wanena kuti: “Lola anthu anga apite kuti akanditumikire. 14 Ukakana, nditumiza miliri yanga yonse pa iwe, pa atumiki ako ndi anthu ako, kuti udziwe kuti palibe wofanana ndi ine padziko lonse lapansi.+ 15 Pofika pano ndikanakhala nditatambasula kale dzanja langa nʼkupha iweyo komanso anthu ako ndi mliri woopsa, ndipo ndikanakufafanizani padziko lapansi. 16 Koma ndakusiya ndi moyo kuti ndikusonyeze mphamvu zanga komanso kuti dzina langa lilengezedwe padziko lonse lapansi.+ 17 Kodi ukudzikuzabe pamaso pa anthu anga, pokana kuwalola kuti achoke? 18 Taona, mawa pa nthawi ngati ino ndigwetsa mvula yamphamvu kwambiri yamatalala, matalala amene sanayambe agwapo mu Iguputo mʼmbiri yonse ya dzikoli mpaka lero. 19 Choncho tumiza atumiki ako kuti asonkhanitse ziweto zako zonse ndi zinthu zako zonse zimene zili kunja nʼkuzilowetsa mʼmalo otetezeka. Munthu aliyense komanso nyama iliyonse imene idzapezeke kunja osati mʼnyumba, idzafa chifukwa matalalawo adzawagwera.”’”

20 Aliyense amene anachita mantha ndi mawu a Yehova pakati pa atumiki a Farao analowetsa mwamsanga ziweto zake ndi antchito ake mʼnyumba. 21 Koma aliyense amene sanamvere mawu a Yehova anasiya atumiki ake ndi ziweto zake kunja.

22 Tsopano Yehova anauza Mose kuti: “Tambasula dzanja lako nʼkuloza kumwamba kuti matalala agwe mʼdziko lonse la Iguputo,+ kuti agwere anthu, nyama ndi zomera zonse mʼdziko la Iguputo.”+ 23 Ndiyeno Mose anatambasula dzanja lake nʼkuloza kumwamba ndi ndodo yake. Atatero, Yehova anachititsa mabingu ndipo anagwetsa matalala ndi moto* padziko lapansi. Choncho Yehova anapitiriza kugwetsa matalala mʼdziko la Iguputo. 24 Ndipo kunagwa matalala komanso moto unkangʼanima. Kunagwa matalala amphamvu kwambiri amene sanaonekepo nʼkale lonse mʼdziko lonse la Iguputo.+ 25 Matalalawo anawononga china chilichonse mʼdziko lonse la Iguputo. Anapha anthu komanso nyama ndipo anawononga zomera zonse zamʼmunda. Anagwetsanso mitengo yonse yamʼdzikolo.+ 26 Koma kudera la Goseni kokha, kumene kunali Aisiraeli, sikunagwe matalala.+

27 Kenako Farao anatumiza atumiki ake kukaitana Mose ndi Aroni nʼkuwauza kuti: “Tsopano ndachimwa. Yehova ndi wolungama, koma ine ndi anthu anga ndife olakwa. 28 Muchonderereni Yehova kuti mabingu ndi matalalawa athe. Mukatero ndikulolani kuti muzipita, ndipo simukhalanso kuno.” 29 Choncho Mose anamuyankha kuti: “Ndikangotuluka mumzinda uno, ndikweza manja anga kwa Yehova. Mabingu asiya ndipo matalala sapitirizanso kugwa kuti mudziwe kuti dziko lapansi ndi la Yehova.+ 30 Koma ndikudziwa kuti ngakhale zimenezi zichitike, inuyo ndi atumiki anu simudzaopa Yehova Mulungu.”

31 Pa nthawi imeneyo mbewu za fulakesi* ndi balere zinawonongeka, chifukwa balere anali atakhwima ndipo fulakesi anali atachita maluwa. 32 Koma tirigu* sanawonongeke, chifukwa amakhwima mochedwa.* 33 Ndiyeno Mose anachoka pamaso pa Farao nʼkutuluka mumzindawo. Kenako anakweza manja ake kwa Yehova, ndipo mabingu ndi matalala zinasiya, mvulanso inasiya kugwa padziko lapansi.+ 34 Farao ataona kuti mvula, matalala ndi mabingu zasiya, anachimwanso ndipo anaumitsa mtima wake,+ iyeyo ndi atumiki ake. 35 Choncho Farao anapitiriza kuumitsa mtima wake ndipo sanalole kuti Aisiraeli apite, mogwirizana ndi zimene Yehova ananena kudzera mwa Mose.+

10 Kenako Yehova anauza Mose kuti: “Pita kwa Farao chifukwa ndalola kuti iye ndi atumiki ake aumitse mitima yawo,+ kuti ndichite zizindikiro zanga pamaso pake.+ 2 Ndachita zimenezi kuti mufotokozere ana anu ndi zidzukulu zanu mmene ndakhaulitsira Iguputo komanso zizindikiro zimene ndachitira Aiguputo.+ Ndipo mudzadziwa kuti ine ndine Yehova.”

3 Choncho Mose ndi Aroni anapita kwa Farao nʼkukamuuza kuti: “Yehova Mulungu wa Aheberi wanena kuti, ‘Kodi upitiriza kukana kundigonjera mpaka liti?+ Lola anthu anga kuti apite kukanditumikira. 4 Ukapitiriza kukana kuti anthu anga apite, mawa ndikutumizira dzombe mʼdziko lako. 5 Dzombelo lidzakuta nthaka yonse ndipo simudzatha kuona dothi. Lidzadya chilichonse chotsalira komanso chilichonse chimene matalala sanawononge. Ndipo lidzadya mitengo yanu yonse imene yayamba kumera.+ 6 Dzombelo lidzadzaza mʼnyumba zanu, mʼnyumba zonse za atumiki anu ndi mʼnyumba za mu Iguputo monse. Lidzadzaza mʼnyumbazi mpaka kufika poti makolo anu ndi makolo a makolo anu sanaonepo chibadwire chawo.’”+ Atatero, Mose anachoka pamaso pa Farao.

7 Kenako atumiki a Farao anamuuza kuti: “Kodi munthu uyu apitiriza kutizunza* mpaka liti? Lolani anthuwa apite kuti akatumikire Yehova Mulungu wawo. Kodi simunazindikirebe kuti Iguputo wawonongeka?” 8 Choncho Farao anaitanitsa Mose ndi Aroni nʼkuwauza kuti: “Pitani, katumikireni Yehova Mulungu wanu. Koma ndi ndani kwenikweni amene apite?” 9 Ndiyeno Mose anati: “Tipita ndi achinyamata athu, achikulire athu, ana athu aamuna ndi ana athu aakazi pamodzi ndi nkhosa ndi ngʼombe zathu,+ chifukwa tikukachitira Yehova chikondwerero.”+ 10 Farao anawauza kuti: “Ngati ndingalole kuti inu pamodzi ndi ana anu mupite, ndiye kuti Yehova alidi ndi inu.+ Ndikudziwa kuti mukufuna kuchita chinachake choipa. 11 Sizitheka! Amuna okha ndi amene apite kukatumikira Yehova, chifukwa ndi zimene munapempha.” Atanena zimenezi, anawachotsa pamaso pa Farao.

12 Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti: “Tambasula dzanja lako nʼkuloza dziko la Iguputo kuti dzombe ligwe mʼdziko lonselo nʼkudya zomera zonse zamʼdzikomo, chilichonse chimene matalala sanawononge.” 13 Zitatero Mose analoza dziko lonse la Iguputo ndi ndodo yake, ndipo Yehova anachititsa mphepo yochokera kumʼmawa kuwomba padziko lonselo, masana onse ndi usiku onse. Mʼmawa kutacha mphepoyo inabweretsa dzombe. 14 Dzombelo linafika mʼdziko lonse la Iguputo nʼkufalikira mʼmadera onse adzikolo+ ndipo linawononga kwambiri.+ Dzombe lambiri ngati limeneli linali lisanagwepo nʼkale lonse ndipo silidzagwanso lambiri ngati limeneli. 15 Dzombelo linakuta nthaka yonse yamʼdzikolo ndipo dziko linachita mdima. Dzombelo linadya zomera zonse zamʼdzikolo ndi zipatso zonse zamʼmitengo zimene sizinawonongeke ndi matalala, moti sipanatsale chobiriwira chilichonse mʼmitengo kapena mʼminda mʼdziko lonse la Iguputo.

16 Ndiyeno Farao anaitanitsa Mose ndi Aroni mwamsanga nʼkuwauza kuti: “Ndachimwira Yehova Mulungu wanu ndiponso ndachimwira inu. 17 Chonde ndikhululukireni tchimo langa ulendo uno wokha, ndipo chondererani Yehova Mulungu wanu kuti andichotsere mliri wakuphawu.” 18 Choncho iwo anachoka pamaso pa Farao ndipo anapita kukachonderera Yehova.+ 19 Atatero Yehova anachititsa kuti mphepo yamphamvuyo iziwomba kuchokera kumadzulo ndipo inatenga dzombelo nʼkukaliponya mʼNyanja Yofiira. Mʼdera lonse la Iguputo simunatsale dzombe ngakhale limodzi. 20 Komabe Yehova analola Farao kuumitsa mtima wake+ moti sanalole kuti Aisiraeli achoke.

21 Kenako Yehova anauza Mose kuti: “Tambasula dzanja lako ndi kuloza kumwamba kuti mʼdziko lonse la Iguputo mugwe mdima wandiweyani.” 22 Nthawi yomweyo, Mose anatambasula dzanja lake nʼkuloza kumwamba ndipo mʼdziko lonse la Iguputo munali mdima wandiweyani kwa masiku atatu.+ 23 Anthu sankatha kuonana ndipo palibe amene anachoka pamalo amene anali kwa masiku atatu. Koma kumene Aisiraeli ankakhala kunkawala.+ 24 Zitatero Farao anaitana Mose nʼkumuuza kuti: “Pitani, katumikireni Yehova.+ Koma nkhosa zanu ndi ngʼombe zanu simupita nazo. Ana anunso mungathe kupita nawo.” 25 Koma Mose anati: “Inuyo mutipatse* nyama zokapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zina, kuti tikazipereke kwa Yehova Mulungu wathu.+ 26 Ziweto zathu tipitanso nazo. Sitidzasiya chiweto* ngakhale chimodzi, chifukwa tikagwiritsa ntchito zina mwa ziweto zimenezi polambira Yehova Mulungu wathu. Koma panopa sitikudziwa kuti tikapereka chiyani polambira Yehova mpaka titakafika kumeneko.” 27 Choncho Yehova analola Farao kuumitsa mtima wake ndipo sanalole kuti Aisiraeli achoke.+ 28 Ndiyeno Farao anauza Mose kuti: “Choka pamaso panga! Uonetsetse kuti usadzaonekerenso pamaso panga, chifukwa tsiku limene ndidzakuonenso udzafa.” 29 Ndipo Mose anayankha kuti: “Monga mwanenera, sindidzaonekeranso pamaso panu.”

11 Choncho Yehova anauza Mose kuti: “Patsala mliri umodzi wokha woti ndigwetsere Farao ndi Iguputo. Kenako adzakulolani kuchoka mʼdziko lino.+ Pokuuzani kuti muchoke, adzachita kukuthamangitsani.+ 2 Tsopano uza anthu kuti mwamuna aliyense ndi mkazi aliyense apemphe kwa munthu wokhala naye pafupi zinthu zasiliva ndi zagolide.”+ 3 Ndiyeno Yehova anachititsa kuti Aiguputo akomere mtima Aisiraeli. Komanso Mose ankalemekezedwa kwambiri mʼdziko la Iguputo, pamaso pa atumiki a Farao ndi pamaso pa Aiguputo onse.

4 Choncho Mose anati: “Yehova wanena kuti, ‘Pakati pa usiku ndilowa mu Iguputo,+ 5 ndipo mwana aliyense woyamba kubadwa mʼdziko la Iguputo adzafa.+ Kuyambira mwana woyamba wa Farao amene wakhala pampando wachifumu, mpaka mwana woyamba wa kapolo wamkazi amene akugwira ntchito pamphero* ndiponso mwana woyamba kubadwa wa nyama iliyonse.+ 6 Mʼdziko lonse la Iguputo mudzakhala kulira kwakukulu kumene sikunachitikepo ndiponso kumene sikudzachitikanso.+ 7 Ngakhale galu sadzauwa aliyense wa Aisiraeli, sadzauwa anthu kapena ziweto zawo, kuti mudziwe kuti Yehova akhoza kuchitira Aisiraeli zinthu zosiyana ndi zimene angachitire Aiguputo.’+ 8 Ndipo atumiki anu onsewa adzabwera kwa ine nʼkundigwadira komanso kundiweramira. Iwo adzanena kuti, ‘Pita, iweyo ndi anthu onse amene amakutsatira.’+ Akadzatero ndidzapitadi.” Atanena mawu amenewa anachoka kwa Farao atakwiya.

9 Kenako Yehova anauza Mose kuti: “Farao sadzakumverani inu.+ Izi zili choncho kuti ndichite zodabwitsa zochuluka mʼdziko la Iguputo.”+ 10 Mose ndi Aroni anachita zodabwitsa zonsezi pamaso pa Farao.+ Koma Yehova analola Farao kuumitsa mtima wake, moti sanalole kuti Aisiraeli achoke mʼdziko lake.+

12 Tsopano Yehova anauza Mose ndi Aroni mʼdziko la Iguputo kuti: 2 “Mwezi uno uzikhala mwezi wanu woyamba pa chaka. Chaka chanu chiziyamba ndi mwezi uno.+ 3 Uzani gulu lonse la Isiraeli kuti, ‘Pa tsiku la 10 la mwezi uno mabanja onse ochokera mwa kholo limodzi adzatenge nkhosa imodziimodzi,+ banja lililonse lidzatenge nkhosa imodzi. 4 Koma ngati banja lili lalingʼono moti silingamalize kudya nkhosa yonseyo, banjalo lidzaitane banja lina loyandikana nalo kuti adzadyere limodzi mʼnyumba mwawo, mogwirizana ndi chiwerengero cha anthu. Muziganizira mmene munthu aliyense amadyera kuti mudziwe kuchuluka kwa nyama imene ikufunika. 5 Nkhosa yanuyo ikhale yopanda chilema,+ yamphongo, yachaka chimodzi. Mungatenge mwana wa nkhosa kapena wa mbuzi. 6 Nkhosayo muisamalire mpaka tsiku la 14 la mwezi uno.+ Kenako banja lililonse la Aisiraeli lidzaphe nkhosa yawo madzulo kuli kachisisira.*+ 7 Adzatenge magazi nʼkuwawaza pamafelemu awiri amʼmbali mwa khomo ndi pafelemu lapamwamba pa chitseko. Adzachite zimenezi panyumba zimene adzadyeremo nkhosayo.+

8 Adzadye nyamayo usiku umenewu.+ Adzaiwotche pamoto ndipo adzaidye pamodzi ndi mikate yopanda zofufumitsa+ ndi masamba owawa.+ 9 Musadzaidye yaiwisi, yowiritsa kapena yophika ndi madzi, koma mudzadye yowotcha pamoto. Mudzawotche mutu wake pamodzi ndi ziboda ndiponso zamʼmimba. 10 Musadzasunge nyama iliyonse kuti ifike mʼmawa. Koma iliyonse yotsala kufika mʼmawa mudzaipsereze pamoto.+ 11 Kudya kwake mudzadye chonchi, mudzakhale mutamanga lamba mʼchiuno mwanu, mutavala nsapato ndiponso mutatenga ndodo mʼdzanja lanu. Muzidzadya mofulumira. Ameneyu ndi Pasika* wa Yehova. 12 Ine ndidzadutsa mʼdziko la Iguputo usiku umenewo nʼkupha mwana aliyense woyamba kubadwa mʼdziko la Iguputo, mwana wa munthu kapena wa chiweto.+ Ndipo ndidzapereka chiweruzo pa milungu yonse ya mu Iguputo.+ Ine ndine Yehova. 13 Magaziwo adzakhala chizindikiro panyumba zimene mudzakhalemo. Ndipo ine ndidzaona magaziwo nʼkukupitirirani, moti mliriwo sudzakugwerani nʼkukuwonongani ndikamadzalanga dziko la Iguputo.+

14 Tsiku limeneli lidzakhala chikumbutso kwa inu, ndipo muzichitira Yehova chikondwerero mʼmibadwo yanu yonse. Limeneli ndi lamulo mpaka kalekale, kuti muzichita chikondwerero chimenechi. 15 Muzidya mkate wopanda zofufumitsa kwa masiku 7.+ Pa tsiku loyamba muzichotsa mʼnyumba zanu ufa wokanda wokhala ndi zofufumitsa chifukwa aliyense wodya mkate wokhala ndi zofufumitsa, kuchokera pa tsiku loyamba kukafika pa tsiku la 7, munthu wochita zimenezi aziphedwa kuti asakhalenso mu Isiraeli. 16 Pa tsiku loyamba muzidzachita msonkhano wopatulika, ndipo pa tsiku la 7 muzidzachitanso msonkhano wina wopatulika. Masiku amenewa musamadzagwire ntchito.+ Koma chakudya choti munthu aliyense adye, chimenecho chokha muzidzaphika.

17 Muzidzachita Chikondwerero cha Mikate Yopanda Zofufumitsa,+ chifukwa pa tsiku limeneli ndidzatulutsa makamu anu mʼdziko la Iguputo. Muzidzasunga tsiku limeneli mʼmibadwo yanu yonse. Limeneli ndi lamulo mpaka kalekale. 18 Mʼmwezi woyamba, tsiku la 14 la mwezi umenewo, madzulo muzidzadya mikate yopanda zofufumitsa, mpaka kukafika madzulo a tsiku la 21 mwezi womwewo.+ 19 Kwa masiku 7 mʼnyumba zanu musamadzapezeke ufa wokanda wokhala ndi zofufumitsa, chifukwa aliyense amene wadya chakudya chokhala ndi zofufumitsa, kaya ndi mlendo kapena mbadwa ya Isiraeli,+ munthu ameneyo adzaphedwa kuti asakhalenso pagulu la Isiraeli.+ 20 Musamadzadye chilichonse chokhala ndi zofufumitsa. Mʼnyumba zanu zonse muzidzadya mikate yopanda zofufumitsa.’”

21 Mwamsanga, Mose anaitana akulu onse a Isiraeli+ nʼkuwauza kuti: “Pitani mukasankhire mabanja anu onse ana a ziweto* nʼkuwapha kuti ikhale nsembe ya Pasika. 22 Mukatero mukatenge kamtengo ka hisope* nʼkukaviika mʼbeseni la magazi nʼkuwawaza pafelemu lapamwamba pa chitseko, ndipo ena mwa magaziwo muwawaze pamafelemu awiri amʼmbali mwa khomo. Aliyense asadzatuluke mʼnyumba yake mpaka mʼmawa. 23 Ndiyeno Yehova akamadzapita kukapha Aiguputo ndi mliri, nʼkuona magazi pamafelemu apamwamba pa zitseko zanu ndi mafelemu awiri amʼmbali mwa khomo, Yehova adzapitirira khomo limenelo ndipo sadzalola mliri wa imfa kulowa mʼnyumba zanu.+

24 Choncho muzichita chikondwerero chimenechi. Limeneli ndi lamulo kwa inu ndi kwa ana anu mpaka kalekale.+ 25 Ndipo muzidzachita mwambo umenewu+ mukadzalowa mʼdziko limene Yehova analonjeza kuti adzakupatsani. 26 Ndiyeno ana anu akadzakufunsani kuti, ‘Nʼchifukwa chiyani timachita mwambo umenewu?’+ 27 mudzawauze kuti, ‘Umenewu ndi mwambo wopereka nsembe ya Pasika kwa Yehova, amene anadumpha nyumba za Aisiraeli mu Iguputo pamene ankapha Aiguputo ndi mliri, koma anapulumutsa mabanja athu.’”

Atatero, anthuwo anagwada nʼkuweramira pansi. 28 Choncho Aisiraeli anachoka nʼkukachita mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose ndi Aroni.+ Anachitadi zomwezo.

29 Ndiyeno pakati pa usiku, Yehova anapha mwana aliyense woyamba kubadwa mʼdziko la Iguputo.+ Kuyambira mwana woyamba wa Farao, amene anali pampando wachifumu, mpaka mwana woyamba wa mkaidi amene anali mʼndende, ndiponso mwana aliyense woyamba kubadwa wa nyama.+ 30 Zitatero Farao, atumiki ake onse ndi Aiguputo onse anadzuka usiku umenewo. Ndipo anthu anayamba kulira kwambiri mʼdziko lonse la Iguputo, chifukwa panalibe banja ngakhale limodzi limene linalibe maliro.+ 31 Usiku womwewo Farao anaitanitsa Mose ndi Aroni+ nʼkuwauza kuti: “Nyamukani, chokani pakati pa anthu anga, inuyo ndi Aisiraeli ena onse. Pitani, katumikireni Yehova monga momwe mwanenera.+ 32 Mutengenso nkhosa ndi ngʼombe zanu monga mwanenera ndipo muzipita.+ Komanso mukandipemphere kwa Mulungu kuti andidalitse.”

33 Ndiyeno Aiguputo anayamba kuumiriza anthuwo kuti achoke mʼdzikolo mofulumira.+ Iwo anati, “chifukwa tonsefe tikungokhala ngati tafa kale!”+ 34 Choncho Aisiraeli ananyamula ufa wokanda wopanda zofufumitsa. Anaunyamulira mʼzokandiramo ufa* pamapewa awo atazikulunga mʼnsalu zawo. 35 Aisiraeli anachita zimene Mose anawauza ndipo anapempha Aiguputo zinthu zasiliva, zagolide komanso zovala.+ 36 Choncho Yehova anachititsa kuti Aiguputo akomere mtima anthu ake, moti Aiguputowo anawapatsa zinthu zonse zimene anapempha ndipo iwo anatenga zinthu zambiri za Aiguputo.+

37 Kenako Aisiraeli ananyamuka ku Ramese+ kupita ku Sukoti.+ Panali amuna oyenda pansi pafupifupi 600,000, osawerengera ana.+ 38 Ndipo gulu la anthu a mitundu yosiyanasiyana*+ linapita limodzi ndi Aisiraeliwo. Linapitanso ndi nkhosa, mbuzi komanso ngʼombe zambirimbiri. 39 Iwo anayamba kuphika mikate yozungulira yopanda zofufumitsa pogwiritsa ntchito ufa wokanda umene anachoka nawo ku Iguputo uja. Ufawo unalibe zofufumitsa chifukwa anawauza kuti achoke ku Iguputo mofulumira kwambiri moti sanathe kukonza chakudya chilichonse ponyamuka.+

40 Ndiyeno Aisiraeli amene anakhala ku Iguputo,+ anakhala mʼdziko lachilendo* zaka 430.+ 41 Zaka 430 zimenezi zitatha, pa tsiku lomwe zinathalo, gulu lonse la anthu a Yehova linatuluka mʼdziko la Iguputo. 42 Umenewu ndi usiku umene azidzakondwerera kuti Yehova anawatulutsa mʼdziko la Iguputo. Yehova anafuna kuti Aisiraeli onse, azidzachita chikondwerero chimenechi mʼmibadwo yawo yonse pokumbukira usiku umenewu.+

43 Kenako Yehova anauza Mose ndi Aroni kuti: “Lamulo la Pasika ndi ili: Mlendo* asadye nawo.+ 44 Koma ngati wina ali ndi kapolo wamwamuna amene anamugula ndi ndalama, muzimudula.+ Akadulidwa nayenso angathe kudya. 45 Mlendo wobwera kudzakhala nanu ndiponso waganyu asadye nawo. 46 Muzidyera mʼnyumba imodzi. Musatuluke panja ndi nyama iliyonse komanso musaphwanye fupa lililonse la nyamayo.+ 47 Gulu lonse la Isiraeli lizichita chikondwerero chimenechi. 48 Ngati mlendo amene akukhala nanu akufuna kuchita nawo chikondwerero cha Pasika kwa Yehova, mwamuna aliyense wamʼnyumba yake adulidwe. Akatero angathe kubwera kudzachita nawo chikondwererocho, ndipo ayenera kuonedwa ngati mbadwa ya dzikolo. Koma munthu wosadulidwa asadye nawo.+ 49 Lamulo lililonse lizigwira ntchito mofanana kwa mbadwa ndi kwa mlendo wokhala pakati panu.”+

50 Choncho Aisiraeli onse anachita mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose ndi Aroni. Anachitadi zomwezo. 51 Pa tsiku limeneli, Yehova anatulutsa Aisiraeli onse* mʼdziko la Iguputo.

13 Yehova analankhulanso ndi Mose kuti: 2 “Ndipatulireni* mwana aliyense wamwamuna woyamba kubadwa,* wa munthu ndi wa chiweto, pakati pa Aisiraeli. Ameneyu ndi wanga.”+

3 Kenako Mose anauza anthuwo kuti: “Muzikumbukira tsiku lalero limene mwatuluka mu Iguputo,+ mʼnyumba ya ukapolo, chifukwa Yehova wakutulutsani mʼdzikoli ndi dzanja lake lamphamvu.+ Choncho musadye chilichonse chokhala ndi zofufumitsa. 4 Mukutuluka mu Iguputo lero, mʼmwezi wa Abibu.*+ 5 Yehova akadzakulowetsani mʼdziko la Akanani, Ahiti, Aamori, Ahivi ndi Ayebusi,+ dziko loyenda mkaka ndi uchi,+ limene analumbira kwa makolo anu kuti adzakupatsani,+ muzidzachita mwambo umenewu mʼmwezi uno. 6 Muzidzadya mikate yopanda zofufumitsa kwa masiku 7,+ ndipo pa tsiku la 7 muzidzachita chikondwerero kwa Yehova. 7 Muzidzadya mikate yopanda zofufumitsa kwa masiku 7.+ Musamadzapezeke ndi chilichonse chokhala ndi zofufumitsa.+ Ufa wokanda wokhala ndi zofufumitsa usamadzapezeke pena paliponse mʼdziko lanu. 8 Ndiyeno pa tsiku limenelo mudzauze ana anu kuti, ‘Tikuchita izi chifukwa cha zimene Yehova anatichitira potuluka mu Iguputo.’+ 9 Mwambowu ukhale ngati chizindikiro cholembedwa padzanja lanu ndi pamphumi panu.*+ Uzikukumbutsani kuti muzilankhula za chilamulo cha Yehova. Uzikukumbutsaninso kuti Yehova ndi amene anakutulutsani mʼdziko la Iguputo ndi dzanja lake lamphamvu. 10 Muzitsatira lamulo limeneli pa nthawi yake yoikidwiratu chaka ndi chaka.+

11 Yehova akadzakulowetsani mʼdziko la Akanani, limene analumbira kuti adzalipereka kwa inu ndi makolo anu,+ 12 muzidzapereka kwa Yehova mwana aliyense wamwamuna woyamba kubadwa,* wa munthu komanso wa chiweto. Chachimuna chilichonse ndi cha Yehova.+ 13 Mwana aliyense woyamba kubadwa wa bulu muzimuwombola ndi nkhosa, koma ngati simungamuwombole, muzimuthyola khosi. Ndipo mwana wanu aliyense wamwamuna woyamba kubadwa muzimuwombola.+

14 Ndiyeno mʼtsogolo ana anu akadzakufunsani kuti, ‘Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani?’ mudzawayankhe kuti, ‘Yehova anatitulutsa ndi dzanja lake lamphamvu mu Iguputo, mʼnyumba ya ukapolo.+ 15 Farao atakana mouma mtima kuti tichoke,+ Yehova anapha mwana woyamba kubadwa aliyense mʼdziko la Iguputo, kuyambira mwana woyamba kubadwa wa munthu mpaka mwana woyamba kubadwa wa nyama.+ Nʼchifukwa chake tikupereka nsembe kwa Yehova ana onse a nyama oyamba kubadwa* ndiponso tikuwombola mwana wathu wamwamuna aliyense woyamba kubadwa.’ 16 Mwambowu ukhale ngati chizindikiro cholembedwa padzanja lanu komanso pamphumi panu,*+ chifukwa Yehova anatitulutsa mu Iguputo ndi dzanja lake lamphamvu.”

17 Farao atalola kuti Aisiraeli apite, Mulungu sanawadutsitse mʼdziko la Afilisiti ngakhale kuti inali njira yaifupi, chifukwa Mulungu anati: “Anthu angasinthe maganizo akakumana ndi nkhondo ndipo angabwerere ku Iguputo.” 18 Choncho Mulungu anachititsa kuti Aisiraeli adutse njira yaitali yodzera mʼchipululu chapafupi ndi Nyanja Yofiira.+ Koma potuluka mʼdziko la Iguputo, Aisiraeli anayenda mwadongosolo ngati magulu a asilikali. 19 Mose anatenganso mafupa a Yosefe chifukwa Yosefe analumbiritsa ana a Isiraeli kuti: “Ndithudi, Mulungu adzakukumbukirani, ndipo pochoka kuno mudzatenge mafupa anga.”+ 20 Iwo ananyamuka ku Sukoti nʼkukamanga msasa ku Etamu mʼmalire a chipululu.

21 Pofuna kuwatsogolera, Yehova ankayenda patsogolo pawo. Masana ankawatsogolera pogwiritsa ntchito chipilala cha mtambo+ ndipo usiku ankawatsogolera pogwiritsa ntchito chipilala cha moto kuti chiziwaunikira. Choncho ankatha kuyenda masana komanso usiku.+ 22 Chipilala cha mtambo sichinkachoka patsogolo pa anthuwo masana, komanso chipilala cha moto sichinkachoka patsogolo pawo usiku.+

14 Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti: 2 “Uza Aisiraeli kuti abwerere nʼkumanga msasa pafupi ndi Pihahiroti, pakati pa Migidoli ndi nyanja, koma moyangʼanizana ndi Baala-zefoni.+ Mumange msasa wanu pafupi ndi nyanja, patsogolo pa Baala-zefoni. 3 Kenako Farao adzanena kuti, ‘Aisiraeli asokonezeka ndipo akungoyendayenda mʼdziko lathu. Iwo asochera mʼchipululu.’ 4 Ine ndidzalola kuti Farao aumitse mtima wake,+ ndipo adzawathamangira. Ndidzalemekeza dzina langa pogonjetsa Farao ndi gulu lake lonse lankhondo,+ ndipo Aiguputo adzadziwa kuti ine ndine Yehova.”+ Choncho Aisiraeli anachitadi zomwezo.

5 Kenako mfumu ya Iguputo inauzidwa kuti Aisiraeli athawa. Nthawi yomweyo mtima wa Farao ndi atumiki ake unasinthanso ataganizira za Aisiraeli,+ moti anati: “Nʼchifukwa chiyani tachita zimenezi? Nʼchifukwa chiyani talola kuti akapolo athu Aisiraeli achoke?” 6 Choncho anakonzekeretsa magaleta* ake ankhondo nʼkutenganso asilikali ake.+ 7 Anatenga magaleta ake abwino kwambiri 600 ndi magaleta ena onse a Iguputo, ndipo mʼmagaleta onsewo munakwera asilikali. 8 Choncho Yehova analola Farao mfumu ya Iguputo kuumitsa mtima wake, ndipo anathamangira Aisiraeli pamene iwo ankatuluka mʼdzikomo molimba mtima.*+ 9 Aiguputo ankawathamangira,+ ndipo magaleta onse a Farao, asilikali apamahatchi ndi gulu lake lankhondo anawayandikira. Aisiraeliwo anali atamanga msasa mʼmphepete mwa nyanja, pafupi ndi Pihahiroti moyangʼanizana ndi Baala-zefoni.

10 Farao atafika pafupi, Aisiraeli anakweza maso awo ndipo anaona Aiguputo akuwathamangira. Choncho Aisiraeli anachita mantha kwambiri ndipo anayamba kufuulira Yehova.+ 11 Iwo anafunsa Mose kuti: “Kodi watibweretsa kuno kuti tidzafere mʼchipululu muno chifukwa chakuti mu Iguputo mulibe manda?+ Nʼchifukwa chiyani watichitira zimenezi? Nʼchifukwa chiyani watitulutsa mu Iguputo? 12 Kodi zimene tinkakuuza ku Iguputo kuja si zimenezi? Kodi sitinakuuze kuti, ‘Tisiye tizitumikira Aiguputoʼ? Chifukwa ndi bwino kuti tizitumikira Aiguputo kusiyana nʼkuti tifere mʼchipululu.”+ 13 Atatero Mose anauza anthuwo kuti: “Musachite mantha.+ Limbani mtima ndipo muona mmene Yehova akupulumutsireni lero.+ Chifukwa Aiguputo amene mukuwaona lerowa simudzawaonanso mpaka kalekale.+ 14 Yehova adzakumenyerani nkhondo,+ ndipo inu mudzangokhala phee, osachita chilichonse.”

15 Tsopano Yehova anauza Mose kuti: “Nʼchifukwa chiyani ukundidandaulira? Auze Aisiraeli kuti anyamuke. 16 Ndipo iweyo, utenge ndodo yako nʼkutambasula dzanja lako kuloza panyanja kuti nyanjayo igawanike. Ukatero Aisiraeli adutsa pakati panyanja, panthaka youma. 17 Koma ine ndilola kuti Aiguputo aumitse mitima yawo, moti atsatira Aisiraeli panyanjapo. Ndichita zimenezi kuti ndilemekeze dzina langa pogonjetsa Farao, gulu lake lonse lankhondo, magaleta ake ankhondo ndi asilikali ake apamahatchi.+ 18 Ndipo Aiguputo adzadziwa kuti ine ndine Yehova, ndikadzalemekeza dzina langa pogonjetsa Farao, magaleta ake ankhondo ndi asilikali ake apamahatchi.”+

19 Ndiyeno mngelo wa Mulungu woona+ amene ankayenda patsogolo pa Aisiraeli anachoka nʼkupita kumbuyo kwawo. Ndipo chipilala cha mtambo chija chinachoka kutsogolo nʼkukaima kumbuyo kwawo.+ 20 Mtambowo unaima pakati pa Aiguputo ndi Aisiraeli.+ Mbali imodzi unkachititsa mdima, ndipo mbali ina unkawaunikira usiku.+ Choncho gulu la Aiguputo silinayandikire gulu la Aisiraeli usiku wonse.

21 Mose anatambasula dzanja lake nʼkuloza panyanja,+ ndipo Yehova anachititsa kuti mphepo yamphamvu yakumʼmawa igawe nyanjayo usiku wonse nʼkuumitsa pansi pake.+ Choncho madziwo anagawanika.+ 22 Zitatero Aisiraeli anadutsa pakati pa nyanja, panthaka youma,+ madziwo ataima ngati khoma kudzanja lawo lamanja ndi lamanzere.+ 23 Ndiyeno Aiguputo anawathamangira, ndipo mahatchi onse a Farao, magaleta ake ankhondo ndi asilikali ake apamahatchi anayamba kuwalondola pakati pa nyanja.+ 24 Ndiyeno chakumʼbandakucha,* Yehova ali mʼchipilala cha mtambo ndi cha moto chija,+ anayangʼana gulu la Aiguputo ndipo anachititsa kuti Aiguputowo asokonezeke. 25 Iye ankagulula mawilo a magaleta awo moti ankawayendetsa movutikira. Ndipo Aiguputo ankanena kuti: “Tiyeni tithawe pamaso pa Isiraeli, chifukwa Yehova akuwamenyera nkhondo yolimbana ndi Aiguputo.”+

26 Kenako Yehova anauza Mose kuti: “Tambasula dzanja lako nʼkuloza panyanja kuti madzi abwerere nʼkumiza Aiguputo, magaleta awo ankhondo ndi asilikali awo apamahatchi.” 27 Nthawi yomweyo Mose anatambasula dzanja lake nʼkuloza panyanja, ndipo kutatsala pangʼono kucha nyanjayo inayamba kubwerera mʼmalo mwake. Pamene Aiguputo ankathawa kuti madziwo asawapeze, Yehova anakankhira Aiguputowo pakatikati pa nyanja.+ 28 Madzi amene anabwererawo anamiza magaleta ankhondo, asilikali apamahatchi ndi gulu lonse lankhondo la Farao, amene analondola Aisiraeli mʼnyanjamo.+ Palibe ngakhale mmodzi amene anapulumuka.+

29 Koma Aisiraeli anayenda panthaka youma pakati pa nyanja,+ ndipo madzi anaima ngati khoma kudzanja lawo lamanja ndi lamanzere.+ 30 Choncho pa tsiku limenelo Yehova anapulumutsa Aisiraeli mʼmanja mwa Aiguputo,+ ndipo Aisiraeli anaona Aiguputo atafa mʼmphepete mwa nyanja. 31 Aisiraeli anaonanso mphamvu* zazikulu zimene Yehova anagwiritsa ntchito pogonjetsa Aiguputo. Ndipo Aisiraeli anayamba kuopa Yehova ndi kukhulupirira Yehova ndi mtumiki wake Mose.+

15 Pa nthawiyo Mose ndi Aisiraeli anaimbira Yehova nyimbo iyi:+

“Ndiimbira Yehova, chifukwa walemekezeka kwambiri.+

Mahatchi ndi okwera pamahatchiwo wawaponyera mʼnyanja.+

 2 Mphamvu ndi nyonga zanga ndi Ya,* chifukwa wandipulumutsa.+

Ameneyu ndi Mulungu wanga ndipo ndidzamʼtamanda.+ Ndi Mulungu wa bambo anga,+ ndipo ndidzamulemekeza.+

 3 Yehova ndi msilikali wamphamvu.+ Dzina lake ndi Yehova.+

 4 Magaleta a Farao ndi gulu lake lankhondo wawaponyera mʼnyanja.+

Asilikali odalirika a Farao amira mʼNyanja Yofiira.+

 5 Mafunde amphamvu awakwirira. Amira pansi pa nyanja ngati mwala.+

 6 Dzanja lanu lamanja, inu Yehova, ndi lamphamvu zochuluka.+

Dzanja lanu lamanja, inu Yehova, limaphwanya mdani.

 7 Ndi mphamvu zanu zazikulu mumagwetsa otsutsana nanu.+

Mumatulutsa mkwiyo wanu woyaka moto, ndipo umanyeketsa otsutsana nanu ngati mapesi.

 8 Ndi mpweya wotuluka mʼmphuno mwanu, madzi anaunjikana pamodzi.

Madzi oyenda anaima ngati khoma.

Mafunde amphamvu anaundana pakatikati pa nyanja.

 9 Mdaniyo anati: ‘Ndiwathamangira nʼkuwapeza!

Ndigawa chuma chawo mpaka nditakhutira!

Ndisolola lupanga langa! Dzanja langa liwawononga!’+

10 Mwapemerera mpweya wanu, ndipo nyanja yawamiza.+

Amira mʼmadzi akuya ngati chitsulo cholemera.

11 Ndi mulungu uti amene angafanane nanu, inu Yehova?+

Mumasonyeza kuti ndinu woyera koposa,+ ndani angafanane ndi inu?

Ndinu woyenera kuopedwa ndi kukuimbirani nyimbo zotamanda. Inu mumachita zodabwitsa.+

12 Mwatambasula dzanja lanu lamanja ndipo dziko lapansi lawameza.+

13 Munasonyeza chikondi chanu chokhulupirika potsogolera anthu amene munawawombola.+

Ndi mphamvu zanu, mudzawatsogolera kudziko lanu lopatulika kumene mudzakhala.

14 Anthu adzamva+ ndipo adzanjenjemera.

Anthu okhala ku Filisitiya adzamva ululu.*

15 Pa nthawi imeneyo mafumu a ku Edomu adzachita mantha.

Ndipo olamulira amphamvu a ku Mowabu adzanjenjemera.+

Anthu onse okhala mu Kanani adzataya mtima.+

16 Adzaopa ndipo adzagwidwa ndi mantha aakulu.+

Chifukwa cha dzanja lanu lamphamvu, adzakhala ngati mwala, osachita kanthu.

Mpaka anthu anu atadutsa, inu Yehova,

Mpaka anthu anu amene munawapanga+ atadutsa.+

17 Mudzawabweretsa nʼkuwakhazikitsa mʼphiri limene ndi cholowa chanu.+

Malo okhazikika amene mwakonzeratu kuti mukhalemo, inu Yehova.

Malo opatulika amene manja anu, inu Yehova, anakhazikitsa.

18 Yehova adzalamulira monga mfumu mpaka kalekale.+

19 Mahatchi a Farao, magaleta ake ankhondo ndi asilikali ake apamahatchi atalowa mʼnyanja,+

Yehova wabweza madzi amʼnyanjamo nʼkuwamiza.+

Koma Aisiraeli ayenda panthaka youma pakati pa nyanja.”+

20 Kenako Miriamu, mneneri wamkazi, yemwe anali mchemwali wake wa Aroni, anatenga maseche mʼmanja mwake ndipo akazi ena onse ankamutsatira akuimba maseche nʼkumavina. 21 Pamene amuna ankaimba, Miriamu ankathirira mangʼombe kuti:

“Imbirani Yehova chifukwa walemekezeka kwambiri.+

Mahatchi ndi okwera pamahatchiwo wawaponyera mʼnyanja.”+

22 Kenako Mose anatsogolera Isiraeli kuchoka ku Nyanja Yofiira ndipo analowa mʼchipululu cha Shura. Iwo anayenda mʼchipululumo kwa masiku atatu, koma sanapeze madzi. 23 Iwo anafika ku Mara,+ koma sanathe kumwa madzi a ku Mara chifukwa anali owawa. Nʼchifukwa chake malowo anawapatsa dzina lakuti Mara.* 24 Choncho anthu anayamba kungʼungʼudza motsutsana ndi Mose+ kuti: “Timwa chiyani?” 25 Zitatero Mose anafuulira Yehova+ ndipo Yehova anamusonyeza kamtengo. Mose anaponya kamtengoko mʼmadzi moti madziwo anakhala okoma.

Pamalo amenewo Mulungu anawapatsa lamulo ndi maziko operekera chiweruzo, ndipo kumeneko anawayesa.+ 26 Iye anawauza kuti: “Mukadzamvera ndi mtima wonse mawu a Yehova Mulungu wanu, nʼkuchita zinthu zoyenera pamaso pake ndiponso kumvera malamulo ake ndi kusunga malangizo ake onse,+ sindidzakugwetserani matenda aliwonse amene ndinagwetsera Aiguputo,+ chifukwa ine Yehova ndi amene ndikukuchiritsani.”+

27 Kenako anafika ku Elimu kumene kunali akasupe 12 a madzi ndi mitengo 70 ya kanjedza. Choncho iwo anamanga msasa pamenepo pafupi ndi madzi.

16 Atachoka ku Elimu, gulu lonse la Aisiraeli linafika mʼchipululu cha Sini chimene chili pakati pa Elimu ndi Sinai.+ Anafika kumeneko pa tsiku la 15 la mwezi wachiwiri atachoka mʼdziko la Iguputo.

2 Mʼchipululumo gulu lonse la Aisiraeli linayamba kungʼungʼudzira Mose ndi Aroni.+ 3 Aisiraeliwo ankauza Mose ndi Aroni kuti: “Zikanakhala bwino dzanja la Yehova likanatiphera mʼdziko la Iguputo, kumene tinkadya nyama+ ndi mkate nʼkukhuta. Mʼmalomwake mwatibweretsa mʼchipululu muno kuti muphetse mpingo wonsewu ndi njala.”+

4 Kenako Yehova anauza Mose kuti: “Ndikugwetserani chakudya kuchokera kumwamba ngati mvula,+ ndipo aliyense azitola muyezo womukwanira pa tsikulo.+ Ndikuchita izi kuti ndiwayese kuti ndione ngati angatsatire chilamulo changa kapena ayi.+ 5 Koma pa tsiku la 6,+ azitola muyezo wowirikiza kawiri zimene amatola tsiku ndi tsiku+ ndipo azikonzeratu zimene atolazo.”

6 Choncho Mose ndi Aroni anauza Aisiraeli onse kuti: “Madzulo ano mudziwa kuti Yehova ndi amene anakutulutsani mʼdziko la Iguputo.+ 7 Mawa mʼmawa mudzaona ulemerero wa Yehova chifukwa wamva kungʼungʼudza kwanu kotsutsana ndi Yehovayo. Ife ndi ndani kuti muzitingʼungʼudzira?” 8 Ndiyeno Mose anapitiriza kuti: “Yehova akakupatsani nyama yoti mudye madzulo ano ndi mkate wokwanira mʼmawa, muona kuti Yehova wamva kungʼungʼudza kwanu kotsutsana naye. Ife ndi ndani? Kungʼungʼudza kwanu si kotsutsana ndi ife, koma nʼkotsutsana ndi Yehova.”+

9 Choncho Mose anauza Aroni kuti: “Uza gulu lonse la Aisiraeli kuti, ‘Bwerani pamaso pa Yehova, chifukwa wamva kungʼungʼudza kwanu.’”+ 10 Ndiyeno Aroni atangomaliza kulankhula ndi gulu lonse la Aisiraeli, iwo anatembenuka nʼkuyangʼana kuchipululu. Ndipo kenako ulemerero wa Yehova unaonekera mumtambo.+

11 Yehova anauzanso Mose kuti: 12 “Ndamva kungʼungʼudza kwa Aisiraeli.+ Ndiye uwauze kuti, ‘Madzulo kuli kachisisira* mudzadya nyama ndipo mʼmawa mudzadya mkate nʼkukhuta.+ Pamenepo mudzadziwa kuti ine ndine Yehova Mulungu wanu.’”+

13 Choncho madzulo amenewo kunabwera zinziri zimene zinakuta msasa wonse,+ ndipo mʼmawa kunachita mame kuzungulira msasa wonsewo. 14 Mame aja atauma, panthaka yamʼchipululumo panapezeka tinthu topyapyala ndi tolimba koma tosalala+ ngati madzi amene aundana panthaka. 15 Aisiraeli ataona tinthu timeneti anayamba kufunsana kuti: “Nʼchiyani ichi?” chifukwa sankadziwa kuti chinali chiyani. Mose anawauza kuti: “Ndi chakudya chimene Yehova wakupatsani.+ 16 Yehova walamula kuti, ‘Aliyense atole chakudya chimenechi mogwirizana ndi mmene amadyera. Munthu aliyense muzimutolera muyezo wa omeri*+ imodzi mogwirizana ndi chiwerengero cha anthu amene ali mutenti yanu.’” 17 Choncho Aisiraeli anayamba kutola chakudyacho, ena anatola chambiri koma ena anatola chochepa. 18 Akayeza chakudyacho pamuyezo wa omeri, munthu amene anatola chambiri sichinamutsalire ndipo amene anatola chochepa sichinamuperewere.+ Aliyense anatola mogwirizana ndi mmene amadyera.

19 Ndiyeno Mose anawauza kuti: “Aliyense asasiye chakudyachi mpaka mʼmawa.”+ 20 Koma iwo sanamvere Mose. Anthu ena atasiya chakudyacho mpaka mʼmawa, chinatuluka mphutsi nʼkuyamba kununkha, moti Mose anawakalipira kwambiri. 21 Mʼmawa uliwonse iwo ankatola chakudyacho, aliyense mogwirizana ndi mmene amadyera. Dzuwa likatentha, chakudyacho chinkasungunuka.

22 Pa tsiku la 6, anthuwo anatola muyezo wowirikiza kawiri,+ munthu aliyense maomeri awiri. Ndiyeno atsogoleri onse a gulu la Aisiraeli anabwera kwa Mose kudzanena. 23 Ndipo iye anawayankha kuti: “Ndi zimene Yehova wanena. Mawa ndi tsiku lopuma,* ndi sabata lopatulika la Yehova.+ Zimene mungaphike, phikani, ndipo zimene mungawiritse, wiritsani.+ Zotsala zonse muziike pambali nʼkuzisunga mpaka mʼmawa.” 24 Choncho anasungadi chakudyacho mpaka mʼmawa mogwirizana ndi zimene Mose anawalamula, ndipo sichinanunkhe kapena kuchita mphutsi. 25 Ndiyeno Mose anawauza kuti: “Idyani chakudyachi lero, chifukwa lero ndi sabata la Yehova ndipo simukachipeza kunja kwa msasa. 26 Muzitola chakudyachi masiku 6, koma tsiku la 7 ndi Sabata.+ Pa tsiku limeneli sichidzapezeka kunja kwa msasa.” 27 Komabe, pa tsiku la 7 anthu ena anapita kuti akatole chakudyacho, koma sanachipeze.

28 Choncho Yehova anauza Mose kuti: “Kodi anthu inu mupitiriza kukana kusunga malamulo ndi malangizo anga mpaka liti?+ 29 Dziwani kuti Yehova wakupatsani Sabata.+ Nʼchifukwa chake pa tsiku la 6 akukupatsani chakudya cha masiku awiri. Pa tsiku la 7 aliyense azikhala pamalo ake. Munthu asachoke pamalo ake.” 30 Choncho anthuwo anasunga sabata* tsiku la 7.+

31 Nyumba ya Isiraeli inapatsa chakudyacho dzina lakuti “mana.”* Chinali choyera ngati mapira,* ndipo kukoma kwake kunali ngati makeke opyapyala othira uchi.+ 32 Kenako Mose anati: “Yehova walamula kuti, ‘Dzazani muyezo umodzi wa omeri ndi mana kuti asungidwe mʼmibadwo yanu yonse,+ nʼcholinga choti iwo adzaone chakudya chimene ndinakupatsani mʼchipululu nditakutulutsani mʼdziko la Iguputo.’” 33 Ndiyeno Mose anauza Aroni kuti: “Tenga mtsuko ndipo uthiremo mana okwana muyezo umodzi wa omeri nʼkuuika pamaso pa Yehova kuti asungidwe mʼmibadwo yanu yonse.”+ 34 Aroni anaikadi mtsukowo patsogolo pa Umboni*+ kuti manawo asungidwe mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose. 35 Aisiraeli anadya mana kwa zaka 40+ mpaka pamene analowa mʼdziko limene munkakhala anthu.+ Iwo ankadya mana mpaka pamene anafika mʼmalire a dziko la Kanani.+ 36 Miyezo 10 ya omeri inkakwana muyezo umodzi wa efa.*

17 Gulu lonse la Aisiraeli linachoka kuchipululu cha Sini.+ Ulendowo anaugawa mʼzigawo, mogwirizana ndi mmene Yehova anawauzira,+ ndipo anamanga msasa ku Refidimu.+ Koma kumeneko kunalibe madzi akumwa.

2 Ndiyeno anthu anayamba kukangana ndi Mose+ kuti: “Tipatse madzi timwe.” Koma Mose anawafunsa kuti: “Nʼchifukwa chiyani mukukangana ndi ine? Nʼchifukwa chiyani mukupitiriza kuyesa Yehova?”+ 3 Koma anthuwo anali ndi ludzu kwambiri ndipo anapitiriza kungʼungʼudza motsutsana ndi Mose+ kuti: “Nʼchifukwa chiyani unatitulutsa ku Iguputo kuti udzatiphe ndi ludzu limodzi ndi ana athu ndi ziweto zathu?” 4 Choncho Mose anafuulira Yehova kuti: “Nditani nawo anthuwa? Angotsala pangʼono kundiponya miyala!”

5 Kenako Yehova anauza Mose kuti: “Tsogola ndipo utenge ena mwa akulu a Isiraeli komanso ndodo yako imene unamenya nayo mtsinje wa Nailo.+ Uitenge mʼdzanja lako ndipo uziyenda. 6 Tamvera! Ine ndidzatsogola nʼkukaima pathanthwe ku Horebe. Kumeneko ukamenye thanthwelo ndipo padzatuluka madzi amene anthu adzamwe.”+ Mose anachitadi zomwezo pamaso pa akulu a Isiraeli. 7 Choncho iye anatchula malowo kuti Masa*+ ndi Meriba,*+ chifukwa Aisiraeli anakangana ndi Mose komanso chifukwa chakuti anayesa Yehova+ kuti: “Kodi pakati pathu pano, Yehova alipo kapena ayi?”

8 Ndiyeno Aamaleki+ anabwera kudzamenyana ndi Isiraeli ku Refidimu.+ 9 Zitatero Mose anauza Yoswa+ kuti: “Tisankhire amuna ndipo upite nawo kukamenyana ndi Aamaleki. Mawa ndikaima pamwamba pa phiri nditagwira ndodo ya Mulungu woona mʼdzanja langa.” 10 Yoswa anachitadi zimene Mose anamuuza,+ ndipo anamenyana ndi Aamaleki. Mose, Aroni ndi Hura+ anapita pamwamba pa phiri.

11 Ndiyeno Mose akakweza manja ake mʼmwamba, Aisiraeli ankapambana pankhondoyo, koma akangotsitsa manja ake, Aamaleki ankapambana. 12 Manja a Mose atatopa, anatenga mwala ndi kumuikira, ndipo anakhalapo. Aroni ndi Hura anagwira manja ake, wina dzanja lina winanso dzanja lina, moti manja ake anakhalabe okweza mpaka dzuwa kulowa. 13 Choncho Yoswa anagonjetsa Aamaleki ndi anthu amene anali kumbali yawo pogwiritsa ntchito lupanga.+

14 Kenako Yehova anauza Mose kuti: “Lemba zimenezi mʼbuku kuti anthu azidzazikumbukira ndipo umuuze Yoswa kuti, ‘Ndidzafafaniziratu Aamaleki padziko lapansi ndipo sadzakumbukiridwa nʼkomwe.’”+ 15 Choncho Mose anamanga guwa lansembe nʼkulipatsa dzina lakuti Yehova-nisi,* 16 ndipo anati: “Yehova adzamenya nkhondo ndi Aamaleki ku mibadwomibadwo+ chifukwa dzanja lawo laukira mpando wachifumu wa Ya.”+

18 Ndiyeno Yetero, wansembe wa ku Midiyani, apongozi ake a Mose,+ anamva zonse zimene Mulungu anachitira Mose ndi anthu ake Aisiraeli komanso mmene Yehova anawatulutsira ku Iguputo.+ 2 Kenako Yetero apongozi ake a Mose, anatenga Zipora, mkazi wa Mose, amene Mose anali atamutumiza kwawo. 3 Anatenganso ana aamuna awiri a Zipora.+ Mwana wina, Mose anamupatsa dzina lakuti Gerisomu,*+ ndipo anati: “Chifukwa ndakhala mlendo mʼdziko lachilendo.” 4 Mwana winayo anamupatsa dzina lakuti Eliezere,* ndipo anati: “Mulungu wa atate anga ndi amene amandithandiza, chifukwa anandipulumutsa kwa Farao amene ankafuna kundipha.”+

5 Choncho Yetero, apongozi ake a Mose, limodzi ndi ana aamuna a Mose ndi mkazi wake, anapita kwa Mose mʼchipululu, kuphiri la Mulungu woona, kumene anamanga msasa.+ 6 Ndiyeno anatumiza uthenga kwa Mose kuti: “Ine Yetero, mpongozi wako,+ ndikubwera limodzi ndi mkazi wako ndi ana ako awiri.” 7 Nthawi yomweyo Mose anatuluka kukachingamira apongozi ake, ndipo anagwada nʼkuwerama, kenako anawakisa.* Iwo analonjerana, atatero anapita kukalowa mutenti.

8 Mose anafotokozera apongozi akewo zonse zimene Yehova anachitira Farao ndi Iguputo pofuna kuthandiza Isiraeli.+ Anawafotokozera mavuto onse amene anakumana nawo mʼnjira+ komanso mmene Yehova anawapulumutsira. 9 Yetero anasangalala kwambiri atamva zabwino zonse zimene Yehova anachitira Aisiraeli powapulumutsa ku Iguputo.* 10 Ndiyeno Yetero anati: “Yehova atamandike, amene anakupulumutsani ku Iguputo ndiponso kwa Farao, amenenso analanditsa anthuwa kwa Aiguputo omwe ankawazunza. 11 Tsopano ndadziwa kuti Yehova ndi wamkulu kuposa milungu ina yonse,+ chifukwa cha zimene anachitira anthu amene ankachita zinthu modzikuza pamaso pa anthu ake.” 12 Kenako Yetero, apongozi ake a Mose, anabweretsa nsembe yopsereza ndi nsembe zina kwa Mulungu. Ndipo Aroni ndi akulu onse a Isiraeli anabwera nʼkudyera limodzi chakudya ndi apongozi ake a Mose, pamaso pa Mulungu woona.

13 Tsiku lotsatira, Mose anakhala pansi monga mwa masiku onse kuti atumikire anthu monga woweruza, ndipo anthu ankaima pamaso pa Mose kuyambira mʼmawa mpaka madzulo. 14 Apongozi a Mose ataona zonse zimene iye ankachitira anthuwo anati: “Kodi anthuwa ukuchita nawo chiyani? Nʼchifukwa chiyani wangokhala wekha ndipo anthu onsewa aima pamaso pako kuyambira mʼmawa mpaka madzulo?” 15 Mose anayankha apongozi akewo kuti: “Chifukwa anthuwa akumabwera kwa ine kuti adzamve malangizo a Mulungu. 16 Akakhala ndi mlandu pakati pawo akumabwera nawo kwa ine, ndipo ndikumaweruza nʼkuwauza chigamulo cha Mulungu woona ndi malamulo ake.”+

17 Ndiyeno apongozi a Mose anamuuza kuti: “Zimene ukuchitazi si zabwino. 18 Ndithu iwe ndi anthu amene uli nawowa mutopa nazo zimenezi, chifukwa ntchito imeneyi ndi yaikulu kwambiri ndipo sungathe kuigwira wekha. 19 Tsopano mvera zimene ndikufuna kukuuza. Ndikupatsa malangizo ndipo Mulungu adzakhala nawe.+ Iweyo uzilankhula ndi Mulungu woona mʼmalo mwa anthuwa+ komanso uzipititsa milandu kwa Mulungu woona.+ 20 Ndipo uziwaphunzitsa za malangizo ndi malamulo+ komanso kuwauza njira imene ayenera kuyendamo ndi ntchito imene ayenera kugwira. 21 Pakati pa anthuwa, usankhepo amuna oyenerera,+ oopa Mulungu, okhulupirika, odana ndi kupeza phindu mwachinyengo.+ Amenewa uwaike kuti akhale atsogoleri a anthuwa, ndipo pakhale atsogoleri a magulu a anthu 1,000, atsogoleri a magulu a anthu 100, atsogoleri a magulu a anthu 50 ndi atsogoleri a magulu a anthu 10.+ 22 Pakakhala mlandu uliwonse atsogoleri amenewa aziweruza anthuwo. Mlandu ukakhala wovuta azibwera nawo kwa iwe,+ koma mlandu uliwonse waungʼono, aziweruza. Uwalole amunawa kuti azikuthandiza kuchita zimenezi, kuti udzichepetsere ntchito.+ 23 Ukachita zimenezi, ndipo ngati zikugwirizana ndi zimene Mulungu akufuna, pamenepo udzaikwanitsa ntchitoyi komanso anthuwa adzabwerera kwawo akusangalala.”

24 Nthawi yomweyo Mose anamvera zimene apongozi ake anamuuza ndipo anachita zonse zimene ananena. 25 Mose anasankha amuna oyenerera mu Isiraeli monse kuti akhale atsogoleri a anthu. Anasankha atsogoleri a magulu a anthu 1,000, atsogoleri a magulu a anthu 100, atsogoleri a magulu a anthu 50 ndi atsogoleri a magulu a anthu 10. 26 Choncho iwo ankaweruza anthuwo pakakhala mlandu. Mlandu wovuta ankapita nawo kwa Mose,+ koma mlandu uliwonse waungʼono ankauweruza. 27 Kenako Mose anatsanzikana ndi apongozi ake+ ndipo iwo anabwerera kwawo.

19 Mʼmwezi wachitatu kuchokera pamene Aisiraeli anatuluka mʼdziko la Iguputo, tsiku lomwelo* iwo analowa mʼchipululu cha Sinai. 2 Ananyamuka ku Refidimu+ nʼkulowa mʼchipululu cha Sinai ndipo anamanga msasa wawo mʼchipululumo. Aisiraeli anamanga msasawo pafupi ndi phiri la Sinai.+

3 Kenako Mose anakwera mʼphirimo kukaonekera kwa Mulungu woona.+ Ndipo Yehova analankhula naye mʼphirimo kuti: “Ukanene mawu awa kunyumba ya Yakobo kapena kuti kwa Aisiraeli, 4 ‘Inu munaona nokha zimene ndinachitira Aiguputo,+ kuti ndikunyamuleni pamapiko a chiwombankhanga nʼkukubweretsani kwa ine.+ 5 Tsopano mukadzamvera mawu anga mosamala ndi kusunga pangano langa, mudzakhaladi chuma changa chapadera pa anthu onse,+ chifukwa dziko lonse lapansi ndi langa.+ 6 Inuyo mudzakhala ufumu wanga wa ansembe komanso mtundu wanga woyera.’+ Ukanene mawu amenewa kwa Aisiraeli.”

7 Choncho Mose anatsika ndipo anaitanitsa akulu onse a anthu nʼkuwauza mawu onse amene Yehova anamulamula.+ 8 Kenako anthu onse anayankhira pamodzi kuti: “Zonse zimene Yehova wanena tidzachita zomwezo.”+ Nthawi yomweyo Mose anabwerera kwa Yehova nʼkukamuuza zimene anthuwo anayankha. 9 Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti: “Tamvera! Ndibwera kwa iwe mumtambo wakuda kuti anthu azimva ndikamalankhula nawe komanso kuti azikukhulupirira nthawi zonse.” Apa nʼkuti Mose atanena mawu a anthuwo kwa Yehova.

10 Kenako Yehova anauza Mose kuti: “Pita kwa anthu, ukawayeretse lero ndi mawa ndipo achape zovala zawo. 11 Pa tsiku lachitatu adzakhale okonzeka, chifukwa pa tsiku lachitatulo Yehova adzabwera paphiri la Sinai pamaso pa anthu onse. 12 Anthuwo uwaikire malire kuzungulira phiri lonse nʼkuwauza kuti, ‘Samalani kuti musakwere mʼphiri kapena kukhudza mʼmunsi mwake. Aliyense wokhudza phirili adzaphedwa ndithu. 13 Munthu aliyense asadzakhudze wolakwayo, koma adzaponyedwe miyala kapena kulasidwa.* Kaya ndi nyama kapena munthu, adzaphedwa.’+ Koma lipenga la nyanga ya nkhosa likadzalira,+ anthu onse adzayandikire phirilo.”

14 Ndiyeno Mose anatsika mʼphirimo kupita kwa anthu nʼkuyamba kuwayeretsa ndipo iwo anachapa zovala zawo.+ 15 Iye anauza anthuwo kuti: “Pofika tsiku lachitatu mukhale okonzeka. Amuna asagone ndi akazi awo.”*

16 Pa tsiku lachitatu mʼmawa, kunachita mabingu ndi mphezi ndipo mtambo wakuda+ unakuta phiri. Kunamvekanso kulira kwamphamvu kwambiri kwa lipenga la nyanga ya nkhosa, moti anthu onse mumsasawo anayamba kunjenjemera.+ 17 Zitatero Mose anatulutsa anthuwo mumsasa kuti akaime pamaso pa Mulungu woona, ndipo anaima mʼmunsi mwa phirilo. 18 Phiri la Sinai linafuka utsi paliponse, chifukwa chakuti Yehova anabwera paphiripo mʼmoto.+ Utsi wakewo unkakwera kumwamba ngati utsi wa uvuni ndipo phiri lonse linkanjenjemera kwambiri.+ 19 Pamene kulira kwa lipenga la nyanga ya nkhosako kunkapitiriza kukwera, Mose analankhula ndipo Mulungu woona anamuyankha.

20 Choncho Yehova anafika pamwamba pa phiri la Sinai. Kenako Yehova anaitana Mose kuti akwere pamwamba pa phirilo ndipo Mose anakweradi.+ 21 Tsopano Yehova anauza Mose kuti: “Tsika ukachenjeze anthuwo kuti asayese kudumpha malire kufika kwa Yehova kuti amuone, chifukwa onse ochita zimenezi adzafa. 22 Ndipo ansembe amene amayandikira kwa Yehova kawirikawiri adziyeretse, kuti Yehova asawaphe.”+ 23 Kenako Mose anauza Yehova kuti: “Anthuwa sangafike paphiri la Sinai, chifukwa inu munawachenjeza kale pamene munandiuza kuti: ‘Udule malire kuzungulira phiri ndipo muziliona kuti ndi lopatulika.’”+ 24 Koma Yehova anamuuza kuti: “Tsika, ndipo ukabwerenso limodzi ndi Aroni. Koma ansembe ndiponso anthu asadumphe malire nʼkukwera kwa Yehova kuti asawaphe.”+ 25 Choncho Mose anatsika nʼkupita kwa anthuwo ndipo anawauza zonsezi.

20 Kenako Mulungu analankhula mawu awa:+

2 “Ine ndine Yehova Mulungu wanu, amene ndinakutulutsani mʼdziko la Iguputo, mʼnyumba yaukapolo.+ 3 Musakhale ndi milungu ina iliyonse kupatulapo ine.*+

4 Musadzipangire fano kapena chifaniziro cha chinthu chilichonse chakumwamba kapena chapadziko lapansi, kapenanso chamʼmadzi apadziko lapansi.+ 5 Musaziweramire kapena kuzitumikira,+ chifukwa ine Yehova Mulungu wanu, ndine Mulungu amene ndimafuna kuti anthu azidzipereka kwa ine ndekha,+ amene ndimalanga ana, zidzukulu ndi ana a zidzukuluzo, chifukwa cha zolakwa za abambo a anthu odana ndi ine. 6 Koma ndimasonyeza chikondi chokhulupirika kwa anthu mibadwo masauzande amene amandikonda komanso kusunga malamulo anga.+

7 Musagwiritse ntchito dzina la Yehova Mulungu wanu molakwika,+ chifukwa Yehova sadzalekerera aliyense wogwiritsa ntchito dzina Lake molakwika osamulanga.+

8 Muzikumbukira tsiku la Sabata ndipo muziliona kuti ndi lopatulika.+ 9 Muzigwira ntchito zanu zonse kwa masiku 6.+ 10 Koma tsiku la 7 ndi sabata la Yehova Mulungu wanu. Musamagwire ntchito iliyonse inuyo kapena mwana wanu wamwamuna, mwana wanu wamkazi, kapolo wanu wamwamuna, kapolo wanu wamkazi, chiweto chanu kapena mlendo amene akukhala mumzinda wanu.*+ 11 Chifukwa kwa masiku 6 Yehova anapanga kumwamba, dziko lapansi, nyanja ndiponso zonse zimene zili mmenemo ndipo anayamba kupuma pa tsiku la 7.+ Nʼchifukwa chake Yehova anadalitsa tsiku la Sabata ndipo analipanga kukhala lopatulika.

12 Muzilemekeza bambo anu ndi mayi anu+ kuti mukhale ndi moyo nthawi yaitali mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani.+

13 Musaphe munthu.*+

14 Musachite chigololo.+

15 Musabe.+

16 Musapereke umboni wonamizira mnzanu.+

17 Musalakelake nyumba ya mnzanu. Musalakelake mkazi wa mnzanu,+ kapolo wake wamwamuna, kapolo wake wamkazi, ngʼombe yake yamphongo, bulu wake, kapena chinthu chilichonse cha mnzanu.”+

18 Ndiyeno anthu onse ankamva mabingu ndi kulira kwa lipenga la nyanga ya nkhosa, ankaona kungʼanima kwa mphezi ndiponso phiri likufuka utsi. Anthuwo atamva komanso kuona zimenezi ananjenjemera ndipo anaima patali.+ 19 Choncho anthuwo anauza Mose kuti: “Iweyo uzilankhula ndi ife, ndipo ife tizimvetsera, koma Mulungu asalankhule ndi ife kuopera kuti tingafe.”+ 20 Ndiyeno Mose anauza anthuwo kuti: “Musaope, chifukwa Mulungu woona wabwera kuti akuyeseni+ nʼcholinga choti mupitirizebe kumuopa kuti musachimwe.”+ 21 Choncho anthuwo anaimabe patali pomwepo, koma Mose anayandikira mtambo wakuda kumene kunali Mulungu woona.+

22 Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti: “Aisiraeli uwauze kuti, ‘Mwaona nokha kuti ine ndalankhula nanu kuchokera kumwamba.+ 23 Musadzipangire milungu yasiliva komanso milungu yagolide kuti muziilambira pamodzi ndi ine.+ 24 Mundipangire guwa lansembe ladothi, ndipo muziperekapo nsembe zanu zopsereza ndi nsembe zamgwirizano,* nkhosa zanu ndi ngʼombe zanu. Dziwani kuti mʼmalo onse amene ndachititsa dzina langa kukumbukiridwa,+ ndidzabwera kwa inu kumeneko ndipo ndidzakudalitsani. 25 Mukamandipangira guwa lansembe lamiyala, musamamangire miyala yosemedwa ndi zida.+ Chifukwa mukagwiritsa ntchito miyala yosema, ndiye kuti mwadetsa guwalo. 26 Ndipo guwa langa lansembe lisakhale lamasitepe, kuopera kuti pokwera pamenepo maliseche anu angaonekere.’”

21 “Izi ndi zigamulo zoti uwauze:+

2 Mukagula kapolo wa Chiheberi,+ adzakhala kapolo wanu kwa zaka 6, koma mʼchaka cha 7 muzimumasula ndipo azichoka osapereka chilichonse.+ 3 Ngati anabwera ali yekha, adzachokanso ali yekha. Ngati anabwera ndi mkazi, mkazi wakeyo adzapita naye. 4 Ngati mbuye wake wamupatsa mkazi nʼkumuberekera ana aamuna kapena aakazi, mkaziyo ndi ana ake adzakhala a mbuye wake, ndipo mwamunayo adzachoka yekha.+ 5 Koma kapoloyo akanena motsimikiza kuti, ‘Ndimakonda kwambiri mbuye wanga, mkazi wanga ndi ana anga, ndipo sindikufuna kumasulidwa kuti ndichoke,’+ 6 mbuye wakeyo azibwera naye pamaso pa Mulungu woona. Kenako azipita naye pachitseko kapena pafelemu, akatero mbuye wakeyo azimuboola khutu ndi choboolera, ndipo iye adzakhala kapolo wake moyo wake wonse.

7 Munthu akagulitsa mwana wake wamkazi kukhala kapolo, sadzachoka ngati mmene akapolo aamuna amachokera. 8 Ngati mbuye wake sakusangalala naye ndipo sakufuna kuti akhale mkazi wake wamngʼono koma akufuna kumugulitsa kwa munthu wina,* mbuyeyo alibe ufulu womugulitsa kwa anthu a mtundu wina chifukwa wamʼchitira zachinyengo. 9 Koma akamupereka kwa mwana wake wamwamuna, azimupatsa ufulu wonse umene umaperekedwa kwa ana aakazi. 10 Mwana wamwamunayo akakwatira mkazi wina, woyambayo asaleke kumʼpatsa chakudya, zovala komanso kugona naye monga mkazi wake.*+ 11 Koma ngati sakumuchitira zinthu zitatu zimenezi, mkaziyo achoke osapereka ndalama iliyonse.

12 Aliyense amene wamenya munthu mpaka munthuyo kufa ayenera kuphedwa.+ 13 Koma ngati sanamuphe mwadala ndipo Mulungu woona walola kuti zichitike, ndidzakukonzerani malo amene angathawireko.+ 14 Munthu akamupsera mtima mnzake mpaka kumupha mwadala,+ munthuyo aziphedwa. Ngakhale atathawira kuguwa langa lansembe, muzimuchotsa nʼkukamupha.+ 15 Munthu amene wamenya bambo ake kapena mayi ake aziphedwa.+

16 Wina akaba munthu+ nʼkumugulitsa kapena akapezeka ndi munthu wobedwayo,+ aziphedwa.+

17 Aliyense wotemberera bambo ake kapena mayi ake aziphedwa.+

18 Anthu akamakangana, ndiye wina nʼkumenya mnzake ndi mwala kapena chibakera,* mnzakeyo osafa koma wavulala ndipo ali chigonere, muzichita izi: 19 Ngati akutha kudzuka nʼkuyamba kuyendayenda kunja pogwiritsa ntchito ndodo, amene anamʼmenya uja asamalandire chilango. Koma azingopereka malipiro a nthawi imene womenyedwayo wakhala asakugwira ntchito, mpaka mnzakeyo atachiriratu.

20 Munthu akamenya kapolo wake wamwamuna kapena wamkazi ndi ndodo, kapoloyo nʼkumufera, munthuyo azilangidwa ndithu.+ 21 Koma ngati kapoloyo wakhalabe ndi moyo tsiku limodzi kapena masiku awiri, mbuye wakeyo sakuyenera kulangidwa chifukwa kapoloyo anamugula ndi ndalama zake.

22 Ngati amuna akumenyana ndipo avulaza kwambiri mkazi woyembekezera, moti mkaziyo nʼkubereka mwana nthawi yake isanakwane+ koma palibe amene wamwalira,* wovulaza mkaziyo azimulipiritsa mogwirizana ndi zimene mwamuna wa mkaziyo angagamule. Azikapereka malipirowo kudzera kwa oweruza.+ 23 Koma ngati wina wamwalira, pamenepo muzipereka moyo kulipira moyo.+ 24 Wina akavulaza mnzake koopsa, pazikhala diso kulipira diso, dzino kulipira dzino, dzanja kulipira dzanja, phazi kulipira phazi,+ 25 kutentha ndi moto kulipira kutentha ndi moto, chilonda kulipira chilonda, kumenya kulipira kumenya.

26 Ngati munthu wamenya kapolo wake wamwamuna kapena kapolo wake wamkazi padiso nʼkumuvulaza kwambiri, azimasula kapoloyo ndipo azimulola kuchoka ngati malipiro a diso lake.+ 27 Ndipo akagulula dzino la kapolo wake wamwamuna kapena la kapolo wake wamkazi, azimasula kapoloyo ndipo azimulola kuchoka ngati malipiro a dzino lake.

28 Ngati ngʼombe yagunda mwamuna kapena mkazi, munthuyo nʼkumwalira, ngʼombeyo iziponyedwa miyala nʼkuphedwa+ ndipo nyama yake sikuyenera kudyedwa. Zikatero mwiniwake wa ngʼombeyo sakuyenera kulangidwa. 29 Koma ngati ngʼombe inali ndi chizolowezi chogunda anthu ndipo mwiniwake anachenjezedwapo koma sankaiyangʼanira, ndiyeno yapha mwamuna kapena mkazi, ngʼombeyo iziponyedwa miyala ndipo mwiniwakeyo aziphedwanso. 30 Ngati waweruzidwa kuti apereke dipo,* ayenera kulipira mtengo wonse wowombolera moyo wake umene amugamula. 31 Kaya ngʼombeyo inagunda mwana wamwamuna kapena mwana wamkazi, mwiniwake wa ngʼombeyo aziweruzidwa mogwirizana ndi chigamulo chimenechi. 32 Ngati yagunda kapolo wamwamuna kapena wamkazi, mwiniwake azilipira ndalama zokwana masekeli* 30 kwa mbuye wa kapoloyo, ndipo ngʼombeyo iziphedwa mwa kuiponya miyala.

33 Ngati munthu wasiya dzenje losavundikira kapena wakumba dzenje koma osatsekapo ndipo ngʼombe kapena bulu nʼkugweramo, 34 mwiniwake wa dzenjelo azilipira.+ Malipirowo azipereka kwa mwiniwake wa chiwetocho, koma iye azitenga nyama yakufayo. 35 Ngati ngʼombe ya munthu yavulaza nʼkupha ngʼombe ya mnzake, azigulitsa ngʼombe yamoyoyo nʼkugawana ndalamazo komanso azigawana nyama yakufayo. 36 Koma ngati ngʼombeyo inkadziwika kuti ili ndi chizolowezi chogunda zinzake, koma mwiniwake sankaiyangʼanira, azipereka ngʼombe kulipira ngʼombe, ndipo azitenga yakufayo.”

22 “Munthu akaba ngʼombe kapena nkhosa nʼkuipha kapena kuigulitsa, azilipira ngʼombe 5 pa ngʼombe imodzi imene waba, ndi nkhosa 4 pa nkhosa imodzi imene waba.+

2 (Ngati wakuba+ wapezeka akuthyola nyumba kuti abe ndipo wamenyedwa nʼkufa, amene wamuphayo alibe mlandu wa magazi. 3 Koma ngati zachitika dzuwa litatuluka, amene wamuphayo ali ndi mlandu wa magazi.)

Wakuba azilipira ndipo ngati alibe kalikonse, azigulitsidwa kuti alipire zinthu zimene anabazo. 4 Ngati zimene anabazo zapezeka ndi iyeyo zili zamoyo, kaya ndi ngʼombe, bulu kapena nkhosa, azilipira zowirikiza kawiri.

5 Ngati munthu waika ziweto zake kuti zidye mʼmunda wa mpesa kapena wa mbewu zina, ndipo wazilekerera kuti zikadye mʼmunda wa munthu wina, azilipira popereka zokolola zabwino koposa zamʼmunda wake wa mpesa kapena zamʼmunda wake wa mbewu zina.

6 Ngati munthu wayatsa moto, motowo nʼkugwirira zomera zaminga ndipo wafalikira mʼmunda wa munthu wina nʼkuwotcha mitolo yambewu, mbewu zosadula kapena munda wonse, amene anayatsa motowo azilipira mbewu zimene zapsazo.

7 Ngati munthu wapatsa mnzake ndalama kapena katundu wina kuti amusungire, zinthuzo nʼkubedwa mʼnyumba ya mnzakeyo, wakubayo akapezeka azilipira zowirikiza kawiri.+ 8 Ngati wakubayo sanapezeke, azibweretsa mwininyumbayo pamaso pa Mulungu woona*+ kuti zidziwike ngati iyeyo ndi amene waba katundu wa mnzakeyo kapena ayi. 9 Pa milandu yonse yokhudza kutenga chinthu cha mwini popanda chilolezo, kaya ndi ngʼombe, bulu, nkhosa, chovala kapena chilichonse chimene chinasowa chomwe angachiloze kuti, ‘Ichi nʼchanga!’ awiri onsewo mlandu wawo uzifika pamaso pa Mulungu woona.+ Amene Mulungu adzamuweruze kuti ndi wolakwa, azilipira mnzakeyo zowirikiza kawiri.+

10 Ngati munthu wapatsa mnzake bulu, ngʼombe, nkhosa kapena chiweto chilichonse kuti amusungire, ndipo chafa kapena chavulala kwambiri kapenanso chagwidwa popanda munthu kuona zimene zachitika, 11 amene anasunga zinthuzo azilumbira kwa mnzake pamaso pa Yehova kuti sanachite zimenezo pa katundu wa mnzake. Mwiniwake wa katunduyo azivomereza lumbirolo ndipo mnzakeyo asamalipire.+ 12 Koma ngati chiwetocho chinachita kubedwa,* azilipira kwa mwiniwake. 13 Ngati chiwetocho chinaphedwa ndi chilombo, azibweretsa chiweto chakufacho monga umboni. Iye sakuyenera kulipira ngati chiweto chaphedwa ndi chilombo.

14 Koma ngati munthu wabwereka chiweto kwa mnzake ndipo chavulala kwambiri kapena chafa mwiniwake wa chiwetocho palibe, wobwerekayo azilipira. 15 Ngati mwiniwake alipo, wobwerekayo asalipire. Ngati anafunika kupereka ndalama kuti abwereke, adzangopereka ndalama yobwerekera chiwetocho.

16 Mwamuna akanyengerera namwali wosalonjezedwa kukwatiwa nʼkugona naye, azimʼtenga ndithu kukhala mkazi wake atapereka malowolo.+ 17 Bambo a mtsikanayo akakaniratu kupatsa mwamunayo mwana wawo, iye azipereka ndalama zofanana ndi malowolo.

18 Mkazi wamatsenga musamulole kukhala ndi moyo.+

19 Aliyense wogonana ndi nyama, aziphedwa ndithu.+

20 Wopereka nsembe kwa milungu ina osati kwa Yehova yekha, aziphedwa ndithu.+

21 Musamachitire nkhanza mlendo wokhala pakati panu kapena kumʼpondereza,+ chifukwa inunso munali alendo mʼdziko la Iguputo.+

22 Musamazunze mkazi wamasiye kapena mwana wamasiye* aliyense.+ 23 Ngakhale mutamuzunza pangʼono, iye nʼkundilirira, ndidzamva ndithu kulira kwake.+ 24 Mkwiyo wanga udzakuyakirani ndipo ndidzakuphani ndi lupanga, moti akazi anu adzakhala akazi amasiye ndipo ana anu adzakhala ana amasiye.

25 Mukabwereketsa ndalama kwa munthu aliyense wosauka* pakati pa anthu anga, kwa munthu amene ali pafupi ndi inu, musakhale ngati munthu wopereka ngongole yakatapira kwa iye. Musamuuze kuti apereke chiwongoladzanja.+

26 Ukalanda mnzako chovala chake monga chikole cha ngongole,+ uzimubwezera dzuwa likamalowa. 27 Chifukwa chofunda chake nʼchomwecho. Ndi nsalu imene amafunda.+ Nanga afunda chiyani pogona? Ndiyeno akandilirira, ine ndidzamva ndithu, chifukwa ndine wachifundo.+

28 Usatemberere* Mulungu+ kapena mtsogoleri* amene ali pakati pa anthu a mtundu wako.+

29 Musamazengereze kundipatsa nsembe kuchokera pa zokolola zanu zomwe ndi zambiri komanso kuchokera ku vinyo ndi mafuta omwe ndi ochuluka.+ Mwana wanu wamwamuna woyamba kubadwa muzimupereka kwa ine.+ 30 Zimene muzichita ndi mwana woyamba kubadwa wa ngʼombe ndi wa nkhosa yanu ndi izi:+ Azikhala ndi mayi ake masiku 7. Pa tsiku la 8 muzimupereka kwa ine.+

31 Mukhale anthu oyera pamaso panga+ ndipo musadye nyama imene yaphedwa ndi chilombo kuthengo.+ Imeneyo muziponyera agalu.”

23 “Musafalitse nkhani yabodza.+ Musamagwirizane ndi munthu woipa pokhala mboni yokonzera wina zoipa.+ 2 Musamachite zoipa pongotsatira gulu la anthu. Musamalepheretse kuti chilungamo chichitike popereka umboni wabodza chifukwa chofuna kusangalatsa anthu ambiri.* 3 Mukamaweruza mlandu wa munthu wosauka musamamukondere chifukwa choti ndi wosauka.+

4 Mukapeza ngʼombe kapena bulu wa mdani wanu atasochera, muzimubweza ndithu kwa mwiniwake.+ 5 Mukaona bulu wa munthu wodana nanu atagona pansi chifukwa cholemedwa ndi katundu, munthu wodana nanuyo musamamusiye yekha. Muzimuthandiza kumasula katunduyo.+

6 Musamapotoze chigamulo cha munthu wosauka wokhala pakati panu, pa mlandu wake.+

7 Musamagwirizane ndi anthu amene akuneneza munthu mlandu wabodza.* Musamaphe munthu wosalakwa komanso wolungama, chifukwa woipa sindidzamuona kuti ndi wolungama.*+

8 Musamalandire chiphuphu chifukwa chiphuphu chimachititsa khungu anthu amene amaona bwinobwino, ndipo chingapotoze mawu a anthu olungama.+

9 Musamapondereze mlendo amene akukhala nanu. Inu mukudziwa mmene zimakhalira ukakhala mlendo, chifukwa inunso munali alendo mʼdziko la Iguputo.+

10 Kwa zaka 6, muzidzala mbewu mʼminda yanu nʼkukolola mbewuzo.+ 11 Koma chaka cha 7 musamaulime, muziusiya kuti ugonere. Osauka amene ali pakati panu azidya zimene zili mʼmundamo ndipo zimene iwo asiya, nyama zakutchire zidzadya. Muzichita zimenezi ndi munda wanu wa mpesa komanso wa maolivi.

12 Muzigwira ntchito masiku 6. Koma tsiku la 7 musamagwire ntchito, kuti ngʼombe yanu ndi bulu wanu azipuma, komanso kuti mwana wa kapolo wanu wamkazi ndi mlendo apezenso mphamvu.+

13 Muzichita zonse zimene ndakuuzanizi mosamala,+ ndipo musatchule mayina a milungu ina. Asamveke pakamwa panu.+

14 Katatu pa chaka muzindichitira chikondwerero.+ 15 Muzichita Chikondwerero cha Mikate Yopanda Zofufumitsa.+ Muzidya mikate yopanda zofufumitsa masiku 7 pa nthawi imene inaikidwa mʼmwezi wa Abibu*+ mogwirizana ndi zimene ndinakulamulani, chifukwa munatuluka mu Iguputo mʼmwezi umenewu. Ndipo palibe amene ayenera kuonekera kwa ine chimanjamanja.+ 16 Komanso muzichita Chikondwerero cha Zokolola.* Muzikondwerera zipatso zoyamba kucha za mbewu zimene munadzala mʼminda yanu, yomwe ndi ntchito ya manja anu.+ Muzichitanso Chikondwerero cha Kututa* kumapeto kwa chaka, mukamatuta zipatso zamʼmunda, yomwe ndi ntchito ya manja anu.+ 17 Katatu pa chaka, mwamuna aliyense pakati panu azikaonekera pamaso pa Ambuye woona, Yehova.+

18 Mukamapereka magazi a nsembe yanga musawapereke limodzi ndi chilichonse chokhala ndi zofufumitsa. Ndipo nsembe za mafuta zimene mwapereka pazikondwerero zanga zisamagone mpaka mʼmawa.

19 Muzibweretsa kunyumba ya Yehova Mulungu wanu zipatso zoyamba kucha zamʼminda yanu zomwe ndi zabwino kwambiri.+

Musamawiritse mwana wa mbuzi mumkaka wa mayi ake.+

20 Ndikukutumizirani mngelo patsogolo panu+ kuti azikutetezani mʼnjira komanso kukakulowetsani mʼdziko limene ndakukonzerani.+ 21 Muzimumvera ndi kuchita zimene wanena. Musamupandukire, chifukwa sadzakukhululukirani zolakwa zanu,+ popeza dzina langa lili mwa iye. 22 Koma mukamveradi mawu ake ndi kuchitadi zonse zimene ine ndidzanene, ndidzakhala mdani wa adani anu ndipo ndidzalimbana ndi olimbana nanu. 23 Chifukwa mngelo wanga adzakutsogolerani nʼkukulowetsani mʼdziko la Aamori, Ahiti, Aperezi, Akanani, Ahivi ndi Ayebusi ndipo ine ndidzawawononga.+ 24 Musadzaweramire milungu yawo kapena kuitumikira, ndipo musadzatengere zochita zawo.+ Mʼmalomwake, mudzawononge mafano awo komanso kuphwanya zipilala zawo zopatulika.+ 25 Muzitumikira Yehova Mulungu wanu,+ ndipo adzakudalitsani ndi chakudya ndi madzi.+ Ndidzachotsa matenda pakati panu.+ 26 Mʼdziko lanu simudzapezeka mkazi wopititsa padera kapena wosabereka.+ Ndipo ndidzachulukitsa masiku a moyo wanu.*

27 Inu musanafike, ndidzawachititsa kuti azindiopa.+ Ndidzasokoneza anthu onse amene mudzakumane nawo. Ndipo ndidzachititsa kuti adani anu onse agonje nʼkuthawa.*+ 28 Inu musanafike, ndidzachititsa anthuwo mantha*+ ndipo Ahivi, Akanani ndi Ahiti adzathawiratu pamaso panu.+ 29 Sindidzawathamangitsa pamaso panu mʼchaka chimodzi, kuti dzikolo lisakhale bwinja ndiponso kuti zilombo zakutchire zisachuluke nʼkukuvutitsani.+ 30 Ndidzawathamangitsa pamaso panu pangʼonopangʼono mpaka mutaberekana ndi kulanda dzikolo.+

31 Dziko limene ndidzakupatsani lidzayambira ku Nyanja Yofiira mpaka kunyanja ya Afilisiti, ndiponso kuyambira kuchipululu mpaka ku Mtsinje.*+ Ndidzachita zimenezi chifukwa anthu okhala mʼdzikomo ndidzawapereka mʼmanja mwanu ndipo inu mudzawathamangitsa pamaso panu.+ 32 Musamachite pangano ndi iwo kapena milungu yawo.+ 33 Asamakhale mʼdziko lanu kuti asakuchititseni kuti mundichimwire. Mukadzatumikira milungu yawo, udzakhala msampha ndithu kwa inu.”+

24 Kenako Mulungu anauza Mose kuti: “Kwera mʼphiri upite kwa Yehova, iweyo, Aroni, Nadabu, Abihu+ ndi akulu 70 a Isiraeli, ndipo mukagwade chapatali. 2 Mose yekha akayandikire kwa Yehova, koma enawo asakayandikire. Anthu ena onse asakwere mʼphiri.”+

3 Ndiyeno Mose anapita kwa anthu nʼkuwafotokozera mawu onse a Yehova ndi zigamulo zake zonse.+ Atatero anthu onse anayankhira pamodzi kuti: “Mawu onse amene Yehova wanena tidzachita.”+ 4 Choncho Mose analemba mawu onse a Yehova.+ Ndiyeno anadzuka mʼmawa kwambiri nʼkukamanga guwa lansembe ndi zipilala 12 zoimira mafuko 12 a Isiraeli, mʼmunsi mwa phiri. 5 Kenako anatuma Aisiraeli achinyamata ndipo iwo anapereka nsembe zopsereza komanso anapereka ngʼombe kuti zikhale nsembe zamgwirizano+ zoperekedwa kwa Yehova. 6 Ndiyeno Mose anatenga hafu ya magazi nʼkuwaika mʼmbale zolowa, ndipo hafu inayo anawaza paguwa lansembe. 7 Kenako anatenga buku la pangano nʼkuwerengera anthuwo mokweza.+ Zitatero anthuwo anati: “Zonse zimene Yehova wanena tidzachita zomwezo ndipo tidzamumvera.”+ 8 Choncho Mose anatenga magaziwo nʼkuwaza anthuwo,+ ndipo anati: “Awa ndi magazi a pangano limene Yehova wapangana nanu mogwirizana ndi mawu onsewa.”+

9 Mose, Aroni, Nadabu, Abihu ndi akulu 70 a Isiraeli anakwera mʼphirimo, 10 ndipo anaona Mulungu wa Isiraeli.+ Pansi pa mapazi ake pankaoneka ngati miyala ya safiro yoyalidwa bwino, yoyera ngati kumwamba.+ 11 Mulungu sanawononge atsogoleri a Aisiraeli,+ koma iwo anaona masomphenya a Mulungu woona ndipo anadya ndi kumwa.

12 Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti: “Kwera mʼphiri muno ufike kwa ine ndipo ukhalebe momʼmuno. Ndikupatsa miyala yosema imene ndalembapo chilamulo kuti ndiphunzitse anthu.”+ 13 Choncho Mose ndi Yoswa mtumiki wake ananyamuka,+ ndipo Mose anakwera mʼphiri la Mulungu woona.+ 14 Koma Mose anauza akuluwo kuti: “Tidikireni pompano mpaka titabwerako.+ Muli ndi Aroni ndi Hura,+ ndiye aliyense amene ali ndi mlandu wofuna kuweruzidwa azipita kwa iwowa.”+ 15 Kenako Mose anakwera mʼphirimo, mtambo utakuta phirilo.+

16 Ulemerero wa Yehova+ unakhalabe paphiri la Sinai,+ ndipo mtambowo unakuta phirilo kwa masiku 6. Pa tsiku la 7, Mulungu anaitana Mose kuchokera mumtambowo. 17 Kwa Aisiraeli amene ankaona zimenezi, ulemerero wa Yehova unkaoneka ngati moto wolilima pamwamba pa phiri. 18 Kenako Mose analowa mumtambomo nʼkukwera mʼphirimo.+ Mose anakhala mmenemo masiku 40, masana ndi usiku.+

25 Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti: 2 “Uza Aisiraeli kuti apereke zopereka kwa ine. Ulandire zopereka zanga kwa munthu aliyense amene akufunitsitsa kupereka.+ 3 Zopereka zimene ukuyenera kulandira kwa iwo ndi izi: golide,+ siliva,+ kopa,*+ 4 ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wapepo,* ulusi wofiira kwambiri, nsalu zabwino kwambiri ndi ubweya wa mbuzi. 5 Ulandirenso zikopa za nkhosa zonyika mu utoto wofiira, zikopa za akatumbu,* matabwa a mthethe,+ 6 mafuta a nyale,+ basamu wopangira mafuta odzozera+ ndi zofukiza zonunkhira.+ 7 Komanso ulandire miyala ya onekisi ndi miyala ina yoika pa efodi+ ndiponso pachovala pachifuwa.+ 8 Mundipangire malo opatulika, ndipo ndidzakhala pakati panu.+ 9 Mukapange chihema chopatulika ndi ziwiya zake zonse mogwirizana ndendende ndi zimene ndikukusonyeza.+

10 Mupange likasa* la mtengo wa mthethe, masentimita 110* mulitali, masentimita 70 mulifupi ndi masentimita 70 kuchoka pansi kupita mʼmwamba.+ 11 Kenako mulikute ndi golide woyenga bwino.+ Mkati ndi kunja komwe mulikute ndi golide, ndipo mupange mkombero wagolide kuzungulira likasalo.+ 12 Mulipangire mphete 4 zagolide ndi kuziika pamwamba pa miyendo yake 4. Mphete ziwiri zikhale mbali imodzi, ndipo mphete zina ziwiri zikhale mbali inayo. 13 Mupangenso ndodo zonyamulira za mtengo wa mthethe nʼkuzikuta ndi golide.+ 14 Mulowetse ndodo zonyamulirazo mumphete zamʼmbali mwa Likasa zija kuti azinyamulira Likasalo. 15 Ndodo zonyamulirazo zizidzakhala mumphete za Likasalo. Sizikuyenera kuchotsedwamo.+ 16 Mkati mwa Likasamo udzaikemo Umboni umene ndidzakupatse.+

17 Mudzapange chivundikiro chagolide woyenga bwino, masentimita 110 mulitali ndi masentimita 70 mulifupi.+ 18 Mupangenso akerubi awiri agolide. Akhale osula ndipo muwaike kumapeto onse awiri a chivundikirocho.+ 19 Kerubi mmodzi akhale kumbali imodzi ya chivundikirocho ndipo kerubi wina akhale kumbali inayo. 20 Akerubiwo atambasule mapiko awo nʼkuwakweza mʼmwamba ndipo aphimbe chivundikirocho ndi mapiko awo.+ Iwo akhale moyangʼanizana, koma nkhope zawo ziweramire pachivundikiro. 21 Chivundikirocho+ udzachiike pa Likasalo, ndipo mu Likasamo udzaikemo Umboni umene ndidzakupatse. 22 Ine ndidzaonekera kwa iwe pamenepo nʼkulankhula nawe kuchokera pamwamba pa chivundikirocho.+ Ndidzakuuza malamulo onse oti ukauze Aisiraeli kuchokera pakati pa akerubi awiriwo, amene ali pamwamba pa likasa la Umboni.

23 Mupangenso tebulo+ la mtengo wa mthethe, masentimita 90 mulitali, masentimita 45 mulifupi ndi masentimita 70 kuchoka pansi mpaka mʼmwamba.+ 24 Mudzalikute ndi golide woyenga bwino, ndipo mudzapange mkombero wagolide kuzungulira tebulo lonselo. 25 Mupange felemu kuzungulira tebulo lonse, muyezo wake masentimita 7* mulifupi mwake ndipo mupangenso mkombero wagolide pafelemulo. 26 Tebulolo mulipangire mphete 4 zagolide ndi kuziika mʼmakona ake 4 mmene muli miyendo yake 4. 27 Mphetezo zikhale pafupi ndi felemu kuti muzilowa ndodo zonyamulira tebulolo. 28 Mupangenso ndodo zonyamulira za mtengo wa mthethe ndipo muzikute ndi golide. Ndodo zimenezi azinyamulira tebulolo.

29 Mupangenso mbale zake, makapu, mitsuko ndi mbale zolowa zoti azithirira nsembe zachakumwa. Muzipange ndi golide woyenga bwino.+ 30 Ndipo patebulopo muziikapo mkate wachionetsero pamaso panga nthawi zonse.+

31 Kenako mupange choikapo nyale+ chagolide woyenga bwino. Choikapo nyalecho chikhale chinthu chimodzi chosula ndipo chikhale ndi tsinde, thunthu, nthambi, timasamba tamʼmunsi mwa duwa, mphindi ndi maluwa.+ 32 Choikapo nyalecho chikhale ndi nthambi 6. Kumbali ina kukhale nthambi zitatu, ndipo kumbali inayo kukhalenso nthambi zitatu. 33 Panthambi za mbali imodzi, iliyonse ikhale ndi timasamba titatu tamʼmunsi mwa duwa topangidwa ngati maluwa a mtengo wa amondi, ndipo timasambato titsatizane ndi mphindi ndi maluwa. Panthambi za mbali inayo, iliyonse ikhalenso ndi timasamba titatu tamʼmunsi mwa duwa topangidwa ngati maluwa a mtengo wa amondi, ndipo timasambato titsatizane ndi mphindi ndi maluwa. Nthambi 6 zotuluka muthunthu la choikapo nyalecho zikhale zotero. 34 Pathunthu la choikapo nyalecho pakhale timasamba 4 tamʼmunsi mwa duwa topangidwa ngati maluwa a mtengo wa amondi, ndipo timasambato titsatizane ndi mphindi ndi maluwa. 35 Mphindi imodzi ikhale pansi pa nthambi zake ziwiri zoyambirira. Mphindi ina ikhalenso pansi pa nthambi zake ziwiri, ndipo mphindi inanso ikhale pansi pa nthambi zinanso ziwiri. Zikhale choncho ndi nthambi 6 zotuluka muthunthu la choikapo nyale. 36 Choikapo nyale chonsecho, kuphatikizapo mphindi ndi nthambi zake, chikhale chimodzi ndipo chisulidwe ndi golide woyenga bwino.+ 37 Muchipangire nyale 7 ndipo nyalezo zikayatsidwa ziziunikira malo amene ali patsogolo pake.+ 38 Zopanira zake zozimitsira nyale ndi mbale zake zoikamo phulusa la zingwe za nyale, zikhale zagolide woyenga bwino.+ 39 Choikapo nyalecho pamodzi ndi ziwiya zake zonsezi azipange pogwiritsa ntchito golide woyenga bwino wolemera talente imodzi.* 40 Uonetsetse kuti wazipanga motsatira chitsanzo chimene wasonyezedwa mʼphiri.”+

26 “Upange chihema+ pogwiritsa ntchito nsalu 10 zopangira tenti. Nsaluzo zikhale za ulusi wopota wabwino kwambiri, ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wapepo ndi ulusi wofiira kwambiri. Pansaluzo upetepo+ akerubi.+ 2 Nsalu iliyonse ikhale mamita 13* mulitali ndipo mulifupi mwake ikhale mamita awiri. Nsalu zonse muyezo wake ukhale wofanana.+ 3 Ulumikize nsalu 5 kuti ikhale nsalu imodzi yaikulu ndipo uchite chimodzimodzi ndi nsalu 5 zinazo. 4 Kumapeto kwa nsalu imodzi yaikulu, upange zingwe zopota zabuluu zokolekamo ngowe. Uchitenso chimodzimodzi kumapeto kwa nsalu inayo, pamalo amene nsalu ziwirizi zidzalumikizane. 5 Uike zingwe zopota 50 zokolekamo ngowe pansalu imodzi, ndipo uikenso zingwe zopota 50 zokolekamo ngowe mʼmphepete mwa nsalu inayo kuti zikhale moyangʼanizana pamalo olumikizirana. 6 Upangenso ngowe 50 zagolide nʼkulumikiza nsalu za tenti zija ndi ngowezo kuti nsaluzo zikhale chinsalu chimodzi chopangira chihema.+

7 Upangenso nsalu za ubweya wa mbuzi+ zoyala pachihemacho. Nsaluzo zikhale zokwana 11.+ 8 Nsalu iliyonse ikhale mamita 13 mulitali komanso mamita awiri mulifupi. Nsalu zonse 11 muyezo wake ukhale wofanana. 9 Ulumikize nsalu 5 pamodzi komanso ulumikize nsalu 6 pamodzi, kenako upinde nsalu ya 6 imene ili kutsogolo kwa nsalu zolumikizanazo. 10 Uike zingwe zopota 50 zokolekamo ngowe mʼmphepete mwa nsalu yakumapeto kwenikweni kwa nsalu za chihema zolumikizanazo. Uikenso zingwe zopota 50 zokolekamo ngowe mʼmphepete mwa nsalu zina zolumikizana, pomwe magulu awiri a nsalu zomwe zalumikizanazo adzakumane. 11 Upange ngowe 50 zakopa nʼkuzilowetsa mʼzingwe zopota zokolekamo ngowezo, nʼkulumikiza nsaluzo kuti zikhale chinsalu chimodzi chopangira chihema. 12 Kumbuyo kwa chihemacho kukhala nsalu yotsala. Choncho hafu ya nsalu yotsalayo ilendewere mpaka mʼmunsi. 13 Ndipo kumbali iliyonse mulitali mwa chinsalucho, mutsala nsalu yokwana masentimita 45. Nsalu yotsalayo izilendewera mpaka mʼmunsi kuti iphimbe chihemacho.

14 Upangenso chophimba chihemacho cha zikopa za nkhosa zonyika mu utoto wofiira ndi chophimba chinanso pamwamba pake cha zikopa za akatumbu.+

15 Upange mafelemu+ oimika a chihema amatabwa a mthethe.+ 16 Felemu lililonse likhale mamita 4 mulitali mwake, ndipo mulifupi mwake likhale masentimita 70. 17 Felemu lililonse likhale ndi zolumikizira ziwiri zoyandikana. Mafelemu onse a chihema uwapange choncho. 18 Upange mafelemu 20 a mbali yakumʼmwera ya chihemacho.

19 Upange zitsulo 40 zasiliva zokhazikapo mafelemu+ 20 aja. Zitsulo ziwiri zikhale pansi pa felemu lililonse kuti mulowe zolumikizira ziwiri.+ 20 Kumbali ina ya chihemacho, mbali yakumpoto kukhale mafelemu 20, 21 ndi zitsulo zake 40 zasiliva zokhazikapo mafelemu. Zitsulo ziwiri zikhale pansi pa felemu lililonse. 22 Upange mafelemu 6 nʼkuwaika kumbuyo kwa chihemacho, mbali yakumadzulo.+ 23 Ndiyeno upange mafelemu awiri kuti akhale ochirikiza mʼmakona awiri akumbuyo kwa chihemacho. 24 Mafelemu amenewa akhale ndi matabwa awiri ophatikiza kuyambira pansi mpaka pamwamba. Matabwawo alumikizane pamphete yoyamba. Mafelemu awiriwo apangidwe mofanana ndipo akhale ochirikiza mʼmakona. 25 Pakhale mafelemu 8 ndi zitsulo 16 zasiliva zokhazikapo mafelemu. Zitsulo ziwiri zikhale pansi pa felemu lililonse.

26 Upangenso ndodo za mtengo wa mthethe, ndodo 5 zikhale za mafelemu a mbali imodzi ya chihema.+ 27 Ndipo ndodo 5 zikhale za mafelemu a mbali ina ya chihema, ndodo zinanso 5 zikhale za mafelemu akumbuyo kwa chihema, mbali yakumadzulo. 28 Ndodo imene ikudutsa pakati pa mafelemu onse iyambire kumayambiriro mpaka kumapeto.

29 Mafelemuwo uwakute ndi golide,+ ndipo mphete zake zolowetsamo ndodo uzipange ndi golide. Ndodozo uzikute ndi golide. 30 Upange chihemacho motsatira pulani yake imene ndakuonetsa mʼphiri.+

31 Upange katani+ ya ulusi wabuluu, ya ubweya wa nkhosa wapepo, ulusi wofiira kwambiri ndi ulusi wopota wabwino kwambiri. Pakataniyi upetepo akerubi. 32 Katani imeneyi uipachike pazipilala 4 za mtengo wa mthethe zokutidwa ndi golide. Tizitsulo tokolowekapo kataniyi tikhale tagolide. Zipilala zimenezi zikhale pazitsulo 4 zasiliva. 33 Kataniyi uipachike mʼmunsi mwa ngowe zolumikizira nsalu zapamwamba pa chihema, ndipo uike likasa la Umboni+ kuseri kwa kataniyi. Kataniyi ikhale malire a Malo Oyera+ ndi Malo Oyera Koposa.+ 34 Ukatero uike chivundikiro pamwamba pa likasa la Umboni mʼMalo Oyera Koposa.

35 Uike tebulo kunja kwa katani. Uikekonso choikapo nyale+ moyangʼanizana ndi tebulo kumbali yakumʼmwera ya chihemacho. Koma tebulolo uliike mbali yakumpoto. 36 Ndiyeno uwombe nsalu yotchinga* khomo la chihema. Nsaluyo ikhale ya ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wapepo, ulusi wofiira kwambiri ndi ulusi wopota wabwino kwambiri.+ 37 Nsalu yotchinga* khomo la chihema uipangire zipilala 5 za mtengo wa mthethe zokutidwa ndi golide. Tizitsulo tokolowekapo nsaluyo tikhale tagolide. Ndipo upange zitsulo 5 zakopa zokhazikapo zipilalazo.”

27 “Upange guwa lansembe lamatabwa a mthethe,+ mulitali likhale mamita awiri,* ndipo mulifupi likhalenso mamita awiri. Guwalo likhale lofanana muyezo wake mbali zake zonse 4, ndipo kutalika kwake kuchokera pansi mpaka mʼmwamba likhale masentimita 134.+ 2 Upange nyanga mʼmakona ake+ 4. Nyangazo zituluke mʼmakonawo ndipo ulikute ndi kopa.*+ 3 Kenako upange ndowa zake zochotsera phulusa,* mafosholo ake, mbale zake zolowa, mafoloko aakulu ndi zopalira moto zake. Ziwiya zake zonse uzipange ndi kopa.+ 4 Upangenso sefa wa zitsulo zakopa zolukanalukana, ndipo pasefayo upangepo mphete 4 zakopa mʼmakona ake 4. 5 Ulowetse sefayo chapakati pa guwa lansembe, mʼmunsi mwa mkombero. 6 Guwalo ulipangire ndodo zonyamulira za mtengo wa mthethe ndipo uzikute ndi kopa. 7 Ndodo zonyamulirazo uzizilowetsa mumphetezo mʼmbali zonse ziwiri za guwalo polinyamula.+ 8 Upange bokosi lamatabwa losatseka pansi. Lipangidwe mogwirizana ndi mmene ndakusonyezera mʼphiri.+

9 Ndiyeno upange bwalo+ la chihema. Kumbali yakumʼmwera, bwalolo ulitchinge ndi mpanda wa nsalu za ulusi wopota wabwino kwambiri. Mpandawo ukhale mamita 45 mulitali mwake kumbali imodziyo.+ 10 Upangenso zipilala zake 20 ndi zitsulo 20 zakopa zokhazikapo zipilalazo. Tizitsulo ta zipilala tokolowekapo nsalu ndi tolumikizira take tikhale tasiliva. 11 Nsalu yambali yakumpoto kwa mpandawo ikhalenso mamita 45 mulitali mwake, ndipo kukhale zipilala 20 ndi zitsulo 20 zakopa zokhazikapo zipilalazo. Tizitsulo tokolowekapo nsalu ndi tolumikizira take tikhale tasiliva. 12 Mulifupi mwa bwalolo, kumbali yakumadzulo, mpanda wa nsaluwo kutalika kwake ukhale mamita 23, ndipo ukhale ndi zipilala 10 ndi zitsulo 10 zokhazikapo zipilalazo. 13 Ndipo mulifupi mwa bwalolo kumbali yakumʼmawa, kotulukira dzuwa, kukhale mamita 23. 14 Kudzanja lamanja la geti la bwalolo, mpanda wa nsaluwo ukhale mamita 7 kutalika kwake. Kukhale zipilala zitatu ndi zitsulo zitatu zokhazikapo zipilalazo.+ 15 Ndipo kudzanja lamanzere la geti la bwalolo mpanda wa nsaluwo ukhale mamita 7. Kukhale zipilala zitatu ndi zitsulo zitatu zokhazikapo zipilalazo.

16 Pakhomo la bwalolo pakhale nsalu yowomba yokwana mamita 9 mulitali mwake. Ikhale ya ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wapepo, ulusi wofiira kwambiri ndi ulusi wopota wabwino kwambiri.+ Pakhale zipilala 4 ndi zitsulo 4 zokhazikapo zipilalazo.+ 17 Zipilala zonse kuzungulira bwalo lonselo zikhale ndi tolumikizira tasiliva, ndipo tizitsulo tokolowekapo nsalu tikhalenso tasiliva, koma zitsulo zokhazikapo zipilalazo zikhale zakopa.+ 18 Bwalolo mulitali mwake likhale mamita 45,+ mulifupi mwake mamita 23, ndipo kutalika kwake kuchoka pansi mpaka mʼmwamba kukhale mamita atatu. Nsalu zake zikhale za ulusi wopota wabwino kwambiri, ndipo zitsulo zake zokhazikapo zipilala zikhale zakopa. 19 Ziwiya zonse zogwiritsa ntchito pa utumiki wonse wapachihema, zikhomo zake zonse ndi zikhomo zonse za nsalu yampanda wa bwalolo zikhale zakopa.+

20 Ulamule Aisiraeli kuti akupezere mafuta ounikira oyenga bwino kwambiri a maolivi, kuti nyale ziziyaka nthawi zonse.+ 21 Mʼchihema chokumanako,* kunja kwa katani imene ili pafupi ndi Umboni,+ Aroni ndi ana ake azionetsetsa kuti nyale zikuyaka pamaso pa Yehova, kuyambira madzulo mpaka mʼmawa.+ Limeneli ndi lamulo kwa Aisiraeli kuti mibadwo yawo izichita zimenezi mpaka kalekale.”+

28 “Pakati pa Aisiraeli, usankhe Aroni+ mʼbale wako pamodzi ndi ana ake+ Nadabu, Abihu,+ Eleazara komanso Itamara+ kuti atumikire monga ansembe anga. 2 Aroni mʼbale wako umupangire zovala zopatulika kuti zimupatse ulemerero ndi kumʼkongoletsa.+ 3 Ulankhule ndi anthu onse aluso* amene ndinawapatsa mzimu wa nzeru.+ Anthuwo amupangire Aroni zovala zomwe zizisonyeza kuti wayeretsedwa, kuti atumikire monga wansembe wanga.

4 Zovala zoti apange ndi izi: chovala pachifuwa,+ efodi,+ malaya akunja odula manja,+ mkanjo wamandalasi, nduwira+ ndi lamba wapamimba.+ Aroni mʼbale wako ndi ana ake awapangire zovala zopatulikazi, kuti atumikire monga ansembe anga. 5 Anthu alusowo agwiritse ntchito golide, ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wapepo, ulusi wofiira kwambiri ndi nsalu zabwino kwambiri.

6 Apange efodi wopeta ndi golide, ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wapepo, ulusi wofiira kwambiri ndi ulusi wopota wabwino kwambiri.+ 7 Efodiyo akhale ndi nsalu ziwiri za mʼmapewa ndipo azilumikize kutsogolo ndi kumbuyo kwake. 8 Lamba woluka*+ womangira efodi, wolumikiza ku efodiyo akhale wopangidwa ndi nsalu ya efodi yomweyo. Akhale wopangidwa ndi golide, ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wapepo, ulusi wofiira kwambiri ndi ulusi wopota wabwino kwambiri.

9 Utenge miyala iwiri ya onekisi+ nʼkulembapo mayina a ana a Isiraeli mochita kugoba.+ 10 Mayina 6 uwalembe pamwala umodzi ndipo mayina 6 otsalawo uwalembe pamwala winawo potsatira mmene anabadwira. 11 Mmisiri wogoba agobe mayina a ana a Isiraeli pamiyala iwiriyo ngati mmene amagobera chidindo.+ Kenako miyalayo idzaikidwe mʼzoikamo zake zagolide. 12 Udzalowetse miyala iwiriyo pansalu zamʼmapewa za efodi kuti ikhale miyala ya chikumbutso cha ana a Isiraeli.+ Poonekera kwa Yehova, Aroni azidzanyamula mayina awo pansalu ziwiri zamʼmapewa ake kuti chikhale chikumbutso. 13 Upange zoikamo miyala zagolide, 14 ndi matcheni awiri agolide woyenga bwino. Uwapange ngati zingwe zopota+ mwaluso, ndipo ulumikize matcheni okhala ngati zingwewo ku zoikamo miyala.+

15 Uuze munthu waluso lopeta kuti apange chovala pachifuwa chachiweruzo+ ndipo achipange mwaluso mofanana ndi efodi. Achipange ndi golide, ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wapepo, ulusi wofiira kwambiri ndi ulusi wopota wabwino kwambiri.+ 16 Ukachipinda pakati mbali zake zonse 4 zizifanana, mulitali mwake chikhale masentimita 22* ndipo mulifupi mwake masentimita 22. 17 Uikepo miyala ndipo ikhale mʼmizere 4. Mzere woyamba ukhale ndi miyala ya rube, topazi ndi emarodi. 18 Mzere wachiwiri ukhale ndi miyala ya nofeki, safiro ndi yasipi. 19 Mzere wachitatu ukhale ndi miyala ya lesemu,* agate ndi ametusito. 20 Mzere wa 4 ukhale ndi miyala ya kulusolito, onekisi ndi yade. Ndipo iikidwe mʼzoikamo miyala zagolide. 21 Miyalayo uiike malinga ndi mayina a ana 12 a Isiraeli. Mwala uliwonse aulembe mochita kugoba ngati mmene amagobera chidindo ndipo mwala uliwonse ukhale ndi dzina limodzi mwa mayina a mafuko 12.

22 Pachovala pachifuwa upangepo matcheni agolide woyenga bwino, okhala ngati zingwe zopota.+ 23 Upange mphete ziwiri zagolide nʼkuziika pachovala pachifuwa. Mphete ziwirizo uziike mʼmakona awiri a chovala pachifuwacho. 24 Ulowetse zingwe ziwiri zagolide zija mumphete ziwiri zomwe zili mʼmakona a chovala pachifuwa. 25 Ulowetse zingwe ziwirizo pa zoikamo miyala ziwiri zimene zili pansalu zamʼmapewa za efodi chakutsogolo. 26 Upange mphete ziwiri zagolide nʼkuziika mʼmakona awiri a chovala pachifuwa kumbali yamkati yokhudzana ndi efodi.+ 27 Upangenso mphete zina ziwiri zagolide nʼkuziika kutsogolo kwa efodi, mʼmunsi mwa nsalu ziwiri zamʼmapewa, pafupi ndi polumikizira, pamwamba pa lamba woluka* wa efodi.+ 28 Chovala pachifuwacho achimange ndi chingwe chabuluu. Chingwe chimenecho chilowe mumphete za chovala pachifuwa komanso mphete za efodi. Zimenezi zidzathandiza kuti chovala pachifuwacho chisasunthe koma chizikhala pamwamba pa lamba woluka* wa efodi.

29 Aroni azinyamula mayina a ana a Isiraeli pamtima pake, pachovala pachifuwa chachiweruzo, akamalowa mʼMalo Oyera kuti chikhale chikumbutso pamaso pa Yehova nthawi zonse. 30 Udzaike Urimu ndi Tumimu*+ mʼchovala pachifuwa chachiweruzo, ndipo zizikhala pamtima pa Aroni akamakaonekera pamaso pa Yehova. Aroni azinyamula pamtima pake zinthu zogwiritsa ntchito poweruza Aisiraeli akamaonekera kwa Yehova nthawi zonse.

31 Upange malaya odula manja ovala mkati mwa efodi. Uwapange ndi ulusi wabuluu wokhawokha.+ 32 Malayawo akhale otsegula pamwamba pake, pakatikati. Potsegulapo pakhale popenderera mʼmphepete mwake ndi nsalu yowomba. Pakhale potsegula ngati chovala chakunkhondo chamamba achitsulo, kuti chisangʼambike. 33 Mumpendero wake wamʼmunsi upangemo zinthu zooneka ngati makangaza* za ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wapepo ndi ulusi wofiira kwambiri kuzungulira mpenderowo. Upangenso mabelu agolide pakati pa makangazawo kuzungulira mpenderowo. 34 Uziika belu lagolide kenako khangaza, belu lagolide kenako khangaza kuzungulira mpendero wamʼmunsi mwa malaya odula manjawo. 35 Aroni azivala malayawo kuti atumikire, ndipo mabeluwo azimveka iye akamalowa mʼmalo opatulika pamaso pa Yehova komanso akamatuluka, kuti asafe.+

36 Upangenso kachitsulo konyezimira kagolide woyenga bwino ndipo ulembepo mochita kugoba ngati mmene amagobera chidindo, mawu akuti: ‘Yehova ndi Woyera.’+ 37 Kachitsulo kameneko ukamangirire panduwira+ ndi chingwe chabuluu. Kazikhala patsogolo pa nduwirayo. 38 Kachitsuloko kazikhala pamphumi pa Aroni. Munthu akachimwira zinthu zopatulika+ zimene Aisiraeli amaziyeretsa akamazipereka ngati mphatso zopatulika, Aroni aziyankha mlandu wa tchimo limenelo. Kachitsuloko kazikhala pamphumi pake nthawi zonse, kuti azichititsa anthuwo kukhala ovomerezeka pamaso pa Yehova.

39 Uwombe mkanjo wamandalasi ndi ulusi wabwino kwambiri. Upangenso nduwira ya nsalu yabwino kwambiri ndiponso uluke lamba wa mkanjo.+

40 Ana a Aroni uwapangirenso mikanjo, malamba ndi mipango* yokulunga kumutu+ kuti iwapatse ulemerero ndi kuwakongoletsa.+ 41 Uveke Aroni mʼbale wako pamodzi ndi ana ake zinthu zimenezi. Ukatero uwadzoze,+ uwayeretse nʼkuwaika*+ kuti atumikire monga ansembe anga. 42 Uwapangirenso makabudula ansalu ofika* mʼntchafu kuti azibisa maliseche awo.+ 43 Aroni ndi ana ake azivala makabudula amenewa polowa mʼchihema chokumanako kapena popita kuguwa lansembe kukatumikira pamalo oyera kuti asapalamule mlandu nʼkufa. Limeneli ndi lamulo kwa iye ndi mbadwa* zake mpaka kalekale.”

29 “Uchite izi kuti uwayeretse kuti atumikire monga ansembe anga: Utenge ngʼombe yaingʼono yamphongo ndi nkhosa ziwiri zamphongo zopanda chilema.+ 2 Utengenso mkate wopanda zofufumitsa, mkate wozungulira woboola pakati wopanda zofufumitsa, wothira mafuta komanso timitanda ta mkate topyapyala topanda zofufumitsa, topaka mafuta.+ Uzipange ndi ufa wa tirigu wosalala. 3 Zimenezi uziike mʼdengu nʼkuzipereka zili mʼdengu momwemo.+ Uchitenso chimodzimodzi ndi ngʼombe ndi nkhosa ziwiri zija.

4 Ubweretse Aroni ndi ana ake pakhomo la chihema chokumanako,+ ndipo uwasambitse* ndi madzi.+ 5 Kenako utenge zovala+ zija nʼkuveka Aroni. Umuveke mkanjo ndi malaya odula manja a mkati mwa efodi. Umuvekenso efodi ndi chovala pachifuwa komanso umumange lamba* woluka wa efodi mʼchiuno mwake.+ 6 Umuveke nduwira pamutu pake ndipo panduwirapo uikepo chizindikiro chopatulika cha kudzipereka.+ 7 Kenako utenge mafuta odzozera+ nʼkuwathira pamutu pake kuti akhale wodzozedwa.+

8 Ukatero utenge ana ake nʼkuwaveka mikanjo.+ 9 Aroni ndi ana akewo uwamange malamba pamimba. Ana akewo uwakulunge mipango kumutu kwawo ndipo adzakhala ansembe.+ Limeneli ndi lamulo langa mpaka kalekale. Uchite zimenezi kuti uike Aroni ndi ana ake kuti akhale ansembe.*+

10 Kenako ubweretse ngʼombe patsogolo pa chihema chokumanako, ndipo Aroni ndi ana ake aike manja awo pamutu wa ngʼombeyo.+ 11 Ndiyeno ngʼombeyo uiphe pamaso pa Yehova, pakhomo la chihema chokumanako.+ 12 Ukatero utengeko magazi a ngʼombeyo ndi chala chako ndipo uwapake panyanga za guwa lansembe.+ Magazi otsalawo uwathire pansi pa guwa lansembe.+ 13 Kenako utenge mafuta onse+ okuta matumbo, mafuta apachiwindi, impso ziwiri ndi mafuta ake nʼkuzitentha kuti paguwa lansembe pakhale utsi.+ 14 Koma nyama ya ngʼombeyo, chikopa chake ndi ndowe zake uzitenthe ndi moto kunja kwa msasa. Ngʼombeyo ndi nsembe yamachimo.

15 Ndiyeno utenge nkhosa imodzi, ndipo Aroni ndi ana ake aike manja awo pamutu wa nkhosayo.+ 16 Nkhosayo uiphe nʼkutenga magazi ake ndipo uwawaze mbali zonse za guwa lansembelo.+ 17 Nkhosayo uidule ziwaloziwalo. Kenako utsuke matumbo+ ndi ziboda zake nʼkuika chiwalo chilichonse pamodzi ndi chinzake, kuyambira kumiyendo mpaka kumutu. 18 Nkhosa yonseyo uiwotche kuti utsi wake ukwere mʼmwamba kuchokera paguwalo. Imeneyo ndi nsembe yopsereza yoperekedwa kwa Yehova, yakafungo kosangalatsa.*+ Ndi nsembe yowotcha pamoto yoperekedwa kwa Yehova.

19 Kenako utenge nkhosa ina ija, ndipo Aroni ndi ana ake aike manja awo pamutu wa nkhosayo.+ 20 Uphe nkhosayo nʼkutengako magazi ake ndipo uwapake mʼmunsi pakhutu lakumanja la Aroni, ndi mʼmunsi pamakutu akumanja a ana a Aroni. Uwapakenso pazala zawo za manthu kudzanja lamanja ndi pazala zawo zazikulu za mwendo wakumanja, ndipo uwaze magaziwo mbali zonse za guwa lansembe. 21 Ndiyeno utengeko magazi amene ali paguwa lansembe ndi mafuta pangʼono odzozera+ nʼkuwadontheza pa Aroni ndi pazovala zake. Uwadonthezenso pa ana ake ndi zovala zawo kuti Aroni ndi zovala zake ndiponso ana ake ndi zovala zawo akhale oyera.+

22 Ndiyeno pankhosayo utengepo mafuta ndi mchira wa mafuta ndi mafuta okuta matumbo, mafuta apachiwindi, impso ziwiri ndi mafuta ake+ ndi mwendo wakumbuyo wakumanja, chifukwa nkhosayo ndi yowaikira kuti akhale ansembe.+ 23 Mʼdengu la mikate yosafufumitsa limene lili pamaso pa Yehova utengemo mkate wobulungira, mkate wozungulira woboola pakati wothira mafuta ndi mkate wopyapyala. 24 Zonsezi uziike mʼmanja mwa Aroni ndi mʼmanja mwa ana ake, ndipo uziyendetse uku ndi uku monga nsembe yoperekedwa kwa Yehova. 25 Kenako uzitenge mʼmanja mwawo nʼkuziwotcha paguwa lansembe pamwamba pa nsembe yopsereza, kuti zikhale kafungo kosangalatsa* kwa Yehova. Imeneyi ndi nsembe yowotcha pamoto yoperekedwa kwa Yehova.

26 Kenako utenge chidale cha nkhosa yoikira+ Aroni kuti akhale wansembe ndipo uchiyendetse uku ndi uku monga nsembe yoperekedwa kwa Yehova. Imeneyo idzakhale yako. 27 Pankhosa yoikira Aroni ndi ana ake kuti akhale ansembe, upatule chidale cha nsembe yoyendetsa uku ndi uku, ndi mwendo wa gawo lopatulika umene anapereka.+ 28 Zimenezi zikhale za Aroni ndi ana ake mwa lamulo mpaka kalekale. Aisiraeli ayenera kutsatira lamulo limeneli chifukwa ndi gawo lopatulika. Lidzakhala gawo lopatulika loyenera kuperekedwa ndi Aisiraeli.+ Limeneli ndi gawo lawo lopatulika loperekedwa kwa Yehova kuchokera pansembe zawo zamgwirizano.+

29 Zovala zopatulika+ za Aroni zidzagwiritsidwa ntchito ndi ana ake+ obwera mʼmbuyo mwake akadzawadzoza nʼkuwaika kuti akhale ansembe. 30 Wansembe amene adzalowe mʼmalo mwake kuchokera pakati pa ana ake, amene adzalowe mʼchihema chokumanako kukatumikira mʼmalo oyera, azidzavala zovalazo kwa masiku 7.+

31 Kenako udzatenge nkhosa yowaikira kuti akhale ansembe nʼkuwiritsa nyama yake mʼmalo oyera.+ 32 Aroni ndi ana ake adye+ nyama ya nkhosayo ndi mkate umene uli mʼdengu, adyere pakhomo la chihema chokumanako. 33 Adye zinthu zimene aphimbira machimo kuti awaike* kukhala ansembe nʼkuwayeretsa. Koma munthu wamba* asadye nawo, chifukwa ndi zinthu zopatulika.+ 34 Nyama ya nkhosa yowaikira kuti akhale ansembe ndi mkatewo, zikatsala mpaka mʼmawa, uziwotche ndi moto.+ Siziyenera kudyedwa chifukwa ndi zinthu zopatulika.

35 Uchite zimenezi kwa Aroni ndi ana ake malinga ndi zonse zimene ndakulamula. Udzatenga masiku 7 kuti uwaike* kukhala ansembe.+ 36 Uzipereka ngʼombe ya nsembe yamachimo tsiku lililonse kuti iphimbe machimo. Uziyeretsa guwa lansembe ku machimo poliperekera nsembe yophimba machimo, ndipo uzilidzoza kuti likhale loyera.+ 37 Udzatenga masiku 7 poperekera guwa lansembelo nsembe yophimba machimo. Udzaliyeretse kuti likhale guwa lansembe loyera koposa.+ Aliyense wogwira guwa lansembe azikhala woyera.

38 Zimene uzipereka paguwa lansembelo ndi izi: ana a nkhosa a chaka chimodzi, awiri pa tsiku ndipo uzichita zimenezi nthawi zonse.+ 39 Uzipereka mwana wa nkhosa mmodzi mʼmawa, ndipo mwana wa nkhosa winayo madzulo kuli kachisisira.*+ 40 Popereka mwana wa nkhosa woyamba, uzipereka limodzi ndi ufa wosalala, muyezo wake gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa efa,* wothira mafuta oyenga bwino kwambiri okwana gawo limodzi mwa magawo 4 a muyezo wa hini,* ndi gawo limodzi mwa magawo 4 a vinyo wa nsembe yachakumwa. 41 Uzipereka mwana wa nkhosa wachiwiri madzulo kuli kachisisira.* Uzimupereka pamodzi ndi nsembe yambewu komanso nsembe yachakumwa ngati mmene unachitira mʼmawa. Uzipereke kuti zikhale kafungo kosangalatsa,* nsembe yowotcha pamoto yoperekedwa kwa Yehova. 42 Mʼmibadwo yanu yonse, muzipereka nsembe yopsereza imeneyi nthawi zonse pakhomo la chihema chokumanako pamaso pa Yehova, kumene ndidzaonekera kwa inu kuti ndilankhule nanu.+

43 Ndidzaonekera pamenepo kwa Aisiraeli, ndipo malo amenewa adzayeretsedwa ndi ulemerero wanga.+ 44 Ndidzayeretsa chihema chokumanako ndi guwa lansembe. Ndidzayeretsanso Aroni ndi ana ake+ kuti atumikire monga ansembe anga. 45 Ndidzakhala pakati pa Aisiraeli ndipo ndidzakhala Mulungu wawo.+ 46 Iwo adzadziwa kuti ine ndine Yehova Mulungu wawo, amene ndinawatulutsa mʼdziko la Iguputo kuti ndikhale pakati pawo.+ Ine ndine Yehova Mulungu wawo.”

30 “Upange guwa lansembe zofukiza.+ Ulipange ndi matabwa amthethe.+ 2 Mbali zake zonse 4 zikhale zofanana, mulitali mwake likhale masentimita 45,* mulifupi mwake masentimita 45. Ndipo kutalika kwake kuchoka pansi mpaka pamwamba likhale masentimita 90. Nyanga zake azipangire kumodzi ndi guwalo.*+ 3 Ulikute ndi golide woyenga bwino pamwamba pake ndi mʼmbali mwake kuzungulira guwalo komanso nyanga zake. Upange mkombero wagolide kuzungulira guwa lonselo. 4 Upangenso mphete ziwiri zagolide mʼmunsi mwa mkombero kumbali zake ziwiri zoyangʼanizana kuti muzilowa ndodo zonyamulira guwalo. 5 Upangenso ndodo zonyamulira za mtengo wa mthethe ndipo uzikute ndi golide. 6 Guwalo uliike kutsogolo kwa katani imene ili pafupi ndi likasa la Umboni.+ Likhale patsogolo pa chivundikiro chimene chili pamwamba pa Umboni, pomwe ndidzaonekera kwa iwe.+

7 Aroni+ aziwotcha zofukiza zonunkhira+ kuti paguwapo+ pazikhala utsi mʼmawa uliwonse akamasamalira nyale.+ 8 Komanso Aroni akamayatsa nyalezo madzulo, aziwotcha zofukizazo. Zimenezi ndi zofukiza zoyenera kuperekedwa kwa Yehova nthawi zonse mʼmibadwo yanu yonse. 9 Paguwali usaperekerepo zofukiza zosavomerezeka,+ nsembe yopsereza kapena nsembe yambewu, ndipo usathirepo nsembe yachakumwa. 10 Aroni azipaka ena mwa magazi a nyama ya nsembe yamachimo panyanga za guwalo kuti aphimbe machimo+ a nyangazo. Azichita zimenezi kamodzi pa chaka+ mʼmibadwo yanu yonse. Kwa Yehova guwalo ndi lopatulika koposa.”

11 Kenako Yehova anauza Mose kuti: 12 “Ukamachita kalembera wa ana a Isiraeli,+ aliyense azipereka dipo la moyo wake kwa Yehova pa nthawi imene ukuwawerengayo. Azichita zimenezi kuti mliri usawagwere pochita kalemberayo. 13 Anthu onse amene awerengedwa azipereka zinthu izi: hafu ya sekeli* yofanana ndi sekeli yakumalo oyera.*+ Magera* 20 amakwana sekeli imodzi. Hafu ya sekeli ndi chopereka kwa Yehova.+ 14 Aliyense amene wawerengedwa, kuyambira wa zaka 20 kupita mʼtsogolo azipereka chopereka kwa Yehova.+ 15 Mukamapereka kwa Yehova chopereka chophimba machimo kuti muwombole moyo wanu, anthu olemera asapereke zochuluka, ndipo osauka asapereke zosakwana hafu ya sekeli.* 16 Uzilandira ndalama zasiliva zophimbira machimo kwa Aisiraeli nʼkuzipereka kuti zikagwiritsidwe ntchito pa utumiki wapachihema chokumanako. Ndalama zimenezi zidzathandiza kuti Yehova azikumbukira Aisiraeli komanso zidzaphimba machimo anu kuti muwombole moyo wanu.”

17 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 18 “Upange beseni losambira lakopa+ ndi choikapo chake. Ukatero uliike pakati pa chihema chokumanako ndi guwa lansembe ndipo uthiremo madzi.+ 19 Aroni ndi ana ake azisamba mʼmanja ndi mapazi awo pamenepo.+ 20 Akamalowa mʼchihema chokumanako, kapena akamapita kukatumikira paguwa lansembe, kukapereka kwa Yehova nsembe yowotcha pamoto, azisamba kuti asafe. 21 Azisamba mʼmanja ndi mapazi awo kuti asafe. Limeneli ndi lamulo kwa iwo mpaka kalekale, likhale lamulo kwa Aroni ndi ana ake ku mibadwo yawo yonse.”+

22 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 23 “Kenako utenge mafuta onunkhira, abwino kwambiri awa: mule* woundana wokwana masekeli 500, sinamoni wonunkhira bwino hafu ya muyezo wa mule, kapena kuti masekeli 250, ndi kalamasi wonunkhira wokwana masekeli 250. 24 Utengenso kasiya* masekeli 500 ofanana ndi masekeli akumalo oyera*+ komanso hini* imodzi ya mafuta a maolivi. 25 Zinthu zimenezi upangire mafuta ogwiritsa ntchito pa kudzoza kopatulika, mafuta onunkhira osakanizidwa mwaluso.*+ Akhale mafuta ogwiritsa ntchito pa kudzoza kopatulika.

26 Mafuta amenewa udzozere chihema chokumanako,+ likasa la Umboni, 27 tebulo ndi ziwiya zake zonse, choikapo nyale ndi ziwiya zake zonse, guwa lansembe zofukiza, 28 guwa lansembe zopsereza ndi ziwiya zake zonse, komanso beseni ndi choikapo chake. 29 Uziyeretse kuti zikhale zoyera koposa.+ Aliyense wogwira zinthu zimenezi azikhala woyera.+ 30 Kenako udzoze Aroni+ ndi ana ake+ ndipo uwayeretse kuti atumikire monga ansembe anga.+

31 Uuze Aisiraeli kuti, ‘Mafuta awa akhale mafuta anga ogwiritsa ntchito pa kudzoza kopatulika mʼmibadwo yanu yonse.+ 32 Musapake mafuta amenewa pakhungu la munthu aliyense, ndipo musapange mafuta ofanana nawo pogwiritsa ntchito zinthu zopangira mafutawa. Mafuta amenewa ndi opatulika. Apitirizebe kukhala opatulika kwa inu. 33 Aliyense wopanga mafuta ofanana ndi amenewa, ndiponso amene angapake munthu wamba mafutawa, ayenera kuphedwa kuti asakhalenso pakati pa anthu amtundu wake.’”+

34 Kenako Yehova anauza Mose kuti: “Utenge muyezo wofanana wa zinthu zonunkhira izi:+ madontho a sitakate,* onika, mafuta onunkhira a galibanamu ndi lubani* weniweni. 35 Zinthu zimenezi upangire zofukiza.+ Usakanize zonunkhiritsa zimenezi mwaluso,* uthire mchere,+ zikhale zoyera ndi zopatulika. 36 Kenako upere zina mwa zofukiza zimenezi kuti zikhale ufa wosalala kwambiri. Uike wina mwa ufawo patsogolo pa Umboni mʼchihema chokumanako, kumene ndidzaonekera kwa iwe. Zofukiza zimenezi zikhale zopatulika koposa kwa inu. 37 Musapange zofukiza zanuzanu pogwiritsa ntchito zinthu zopangira zofukiza zimenezi.+ Muziona kuti zofukiza zimenezi nʼzopatulika kwa Yehova. 38 Aliyense wopanga zofukiza zofanana ndi zimenezi pofuna kusangalala ndi kafungo kake, aziphedwa kuti asakhalenso pakati pa anthu a mtundu wake.”

31 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 2 “Inetu ndasankha* Bezaleli+ mwana wamwamuna wa Uri, mwana wa Hura wa fuko la Yuda.+ 3 Ndidzamupatsa mzimu wa Mulungu kuti akhale wanzeru, wozindikira komanso wodziwa kupanga zinthu mwaluso pa ntchito iliyonse, 4 kupanga mapulani a mmene angapangire zinthu mwaluso, kupanga zinthu zagolide, zasiliva ndi zakopa, 5 waluso losema miyala ndi kupanga zoikamo miyala+ komanso wodziwa kupanga chilichonse chamatabwa.+ 6 Kuwonjezera pamenepo ine ndaika Oholiabu+ mwana wamwamuna wa Ahisama wa fuko la Dani kuti athandize Bezaleli. Komanso ndaika nzeru mumtima wa anthu onse amene ali ndi luso,* kuti apange zonse zimene ndakulamulazi:+ 7 chihema chokumanako,+ likasa la Umboni,+ chivundikiro+ chimene chili pamwamba pake ndi zipangizo zonse zamʼchihema. 8 Kutinso apange tebulo+ ndi zipangizo zake, choikapo nyale chagolide woyenga bwino ndi zipangizo zake zonse,+ guwa lansembe zofukiza,+ 9 guwa lansembe zopsereza+ ndi zipangizo zake zonse, beseni ndi choikapo chake,+ 10 zovala zolukidwa bwino, zovala zopatulika za Aroni wansembe, zovala za ana ake zoti azivala potumikira monga ansembe,+ 11 mafuta odzozera ndi zofukiza zonunkhira zapamalo opatulika.+ Iwo adzapanga zonse zimene ndakulamula.”

12 Yehova anauzanso Mose kuti: 13 “Uuze Aisiraeli kuti, ‘Muonetsetse kuti mukusunga masiku anga a sabata.+ Chimenechi ndi chizindikiro pakati pa ine ndi inu mʼmibadwo yanu yonse, kuti mudziwe kuti ine Yehova ndakusankhani kukhala opatulika. 14 Muzisunga Sabata chifukwa ndi lopatulika kwa inu.+ Aliyense wosatsatira lamulo lokhudza sabata ayenera kuphedwa ndithu. Munthu aliyense wogwira ntchito pa tsikuli ayenera kuphedwa kuti asakhalenso pakati pa anthu amtundu wake.+ 15 Muzigwira ntchito masiku 6, koma tsiku la 7 likhale sabata lopuma pa ntchito zonse.+ Limeneli ndi tsiku lopatulika kwa Yehova. Aliyense wogwira ntchito pa tsiku la Sabata ayenera kuphedwa. 16 Aisiraeli azisunga Sabata ndipo azichita zimenezi mʼmibadwo yawo yonse. Limeneli ndi pangano mpaka kalekale. 17 Chimenechi nʼchizindikiro pakati pa ine ndi Aisiraeli mpaka kalekale,+ chifukwa mʼmasiku 6, Yehova anapanga kumwamba ndi dziko lapansi, koma pa tsiku la 7 anapuma pa ntchito yake ndipo anasangalala.’”+

18 Ndiyeno atamaliza kulankhula naye paphiri la Sinai, anapatsa Mose miyala iwiri yosema ya Umboni,+ miyala yolembedwa ndi chala cha Mulungu.+

32 Mose ali mʼphirimo, anthu anaona kuti akuchedwa kutsika.+ Choncho anthuwo anasonkhana kwa Aroni nʼkumuuza kuti: “Tipangire mulungu woti atitsogolere,+ chifukwa sitikudziwa zimene zachitikira Mose, amene ankatitsogolera pochoka ku Iguputo.” 2 Ndiyeno Aroni anawauza kuti: “Tengani ndolo zagolide+ zimene avala akazi anu, ana anu aamuna ndi ana anu aakazi, ndipo mubwere nazo kwa ine.” 3 Choncho anthu onse anayamba kuvula ndolo zagolide zimene anavala nʼkuzipereka kwa Aroni. 4 Kenako iye analandira golideyo kuchokera kwa anthuwo ndipo pogwiritsa ntchito chosemera, anapanga fano* la mwana wa ngʼombe.+ Zitatero iwo anayamba kunena kuti: “Uyu ndi Mulungu wanu, Aisiraeli inu, amene anakutulutsani mʼdziko la Iguputo.”+

5 Aroni ataona zimenezi, anamanga guwa lansembe patsogolo pa fanolo. Kenako iye anafuula kuti: “Mawa kuli chikondwerero cha Yehova.” 6 Choncho pa tsiku lotsatira, anthuwo anadzuka mʼmamawa kwambiri nʼkuyamba kupereka nsembe zopsereza ndi zamgwirizano. Atatero, iwo anakhala pansi ndipo anadya ndi kumwa. Kenako anaimirira nʼkuyamba kusangalala.+

7 Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti: “Pita, tsika, chifukwa anthu ako amene unawatsogolera potuluka mʼdziko la Iguputo aja achita zinthu zoipa.+ 8 Apatuka mofulumira panjira imene ndinawalamula kuti aziyendamo.+ Iwo adzipangira fano* la mwana wa ngʼombe. Akuligwadira komanso kupereka nsembe kwa fanolo ndipo akunena kuti, ‘Aisiraeli inu, uyu ndi Mulungu wanu amene anakutsogolerani potuluka mʼdziko la Iguputo.’” 9 Yehova anapitiriza kuuza Mose kuti: “Ndaona kuti anthu amenewa ndi okanika.+ 10 Ndisiye kuti mkwiyo wanga uwayakire ndipo ndiwafafanize, koma iwe ndikupange kukhala mtundu waukulu.”+

11 Kenako Mose anachonderera Yehova Mulungu wake+ kuti: “Nʼchifukwa chiyani inu Yehova mukufuna kuti mkwiyo wanu uyakire anthu anu, pambuyo powatulutsa mʼdziko la Iguputo pogwiritsa ntchito mphamvu zazikulu ndiponso dzanja lamphamvu?+ 12 Mukawawonongatu Aiguputo anena kuti, ‘Anali ndi zolinga zoipa powatulutsa mʼdziko lino. Iye amafuna kuti akawaphe kumapiri nʼkuwafafaniza padziko lapansi.’+ Bwezani mkwiyo wanu woyaka motowo, ndipo sinthani maganizo anu ofuna kubweretsera anthu anu tsoka limeneli. 13 Kumbukirani Abulahamu, Isaki ndi Isiraeli atumiki anu, amene munawalumbirira powauza kuti: ‘Ndidzachulukitsa mbadwa* zanu ngati nyenyezi zakumwamba+ ndipo dziko lonseli limene ndinalisankha, ndidzalipereka kwa mbadwa* zanu, kuti likhale lawo mpaka kalekale.’”+

14 Choncho Yehova anasintha maganizo ake ndipo sanawononge anthu ake ngati mmene ananenera.+

15 Kenako Mose anatembenuka nʼkutsika mʼphirimo atanyamula miyala yosema ya Umboni+ mʼmanja mwake.+ Pamiyalayo analembapo mawu mbali zonse ziwiri. Anawalemba kutsogolo ndi kumbuyo kwake. 16 Miyalayo inapangidwa ndi Mulungu, ndipo mawuwo analembedwapo ndi Mulungu mochita kugoba.+ 17 Yoswa atayamba kumva phokoso la kufuula kwa anthu, anauza Mose kuti: “Kukumveka phokoso la nkhondo kumsasa.” 18 Koma Mose anati:

“Limeneli si phokoso la nyimbo ya kupambana,

Komanso si phokoso la anthu amene akulira chifukwa chogonjetsedwa;

Ndikumva ngati ndi kuimba kwa mtundu wina.”

19 Mose atayandikira msasawo nʼkuona mwana wa ngʼombe+ ndi anthu akuvina, mkwiyo wake unayaka ndipo anaponya pansi miyala ija nʼkuiswa ali mʼmunsi mwa phiri.+ 20 Ndiyeno anatenga mwana wa ngʼombe amene iwo anapanga nʼkumuwotcha pamoto kenako anamupera kuti akhale fumbi.+ Atatero anamwaza fumbilo pamadzi ndipo analamula Aisiraeli kuti amwe.+ 21 Kenako Mose anafunsa Aroni kuti: “Kodi anthuwa akuchitira chiyani kuti uwabweretsere tchimo lalikulu chonchi?” 22 Ndiyeno Aroni anayankha kuti: “Musakwiye mbuyanga. Inuyo mukudziwa bwino kuti anthuwa amakonda kuchita zoipa.+ 23 Choncho anandiuza kuti, ‘Tipangire mulungu woti atitsogolere, chifukwa sitikudziwa zimene zachitikira Mose, amene ankatitsogolera pochoka ku Iguputo.’+ 24 Ndiye ndinawauza kuti, ‘Aliyense amene wavala chinthu chagolide avule nʼkundipatsa.’ Kenako golideyo ndinamuponya pamoto nʼkukhala mwana wa ngʼombeyu.”

25 Mose anaona kuti anthuwo akuchita zinthu motayirira, chifukwa Aroni sanawaletse ndipo anachita zinthu zochititsa manyazi pamaso pa adani awo. 26 Ndiyeno Mose anakaima pageti la msasawo ndipo anati: “Ndani ali kumbali ya Yehova? Abwere kwa ine!”+ Ndipo Alevi onse anapita kwa Mose. 27 Kenako iye anawauza kuti: “Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Aliyense wa inu amange lupanga lake mʼchiuno. Ndiyeno mudutse mkati mwa msasa kuchoka pageti lina kufika pageti lina, ndipo aliyense wa inu aphe mʼbale wake, munthu wokhala naye pafupi ndi mnzake wapamtima.’”+ 28 Alevi anachita zimene Mose anawauza. Choncho pa tsiku limenelo amuna pafupifupi 3,000 anaphedwa. 29 Zitatero Mose anati: “Dziyeretseni* kuti mutumikire Yehova lero, chifukwa aliyense wa inu waukira mwana wake ndi mʼbale wake+ ndipo lero Mulungu akudalitsani.”+

30 Pa tsiku lotsatira, Mose anauza anthuwo kuti: “Mwachita tchimo lalikulu kwambiri. Choncho ndipita kuphiri kwa Yehova kuti mwina ndingakamuchonderere kuti akukhululukireni tchimo lanu.”+ 31 Ndiyeno Mose anabwerera kwa Yehova nʼkunena kuti: “Anthuwa achita tchimo lalikulu. Adzipangira mulungu wagolide!+ 32 Ngati mukufuna akhululukireni tchimo lawo.+ Koma ngati simukufuna, chonde ndifufuteni mʼbuku lanu limene mwalemba.”+ 33 Komabe Yehova anauza Mose kuti: “Amene wandichimwira ndi amene ndimufufute mʼbuku langa. 34 Choncho pita uwatsogolere anthuwa kumalo amene ndakuuza. Taona! Mngelo wanga akhala patsogolo panu,+ ndipo pa tsiku limene ndidzapereke chilango, ndidzawalanga chifukwa cha tchimo lawo.” 35 Ndiyeno Yehova anagwetsera anthuwo mliri chifukwa cha mwana wa ngʼombe amene iwo anamʼpanga kudzera mwa Aroni.

33 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: “Nyamuka, uchoke pano limodzi ndi anthu amene unawatsogolera potuluka mʼdziko la Iguputo. Mupite kudziko limene ndinalumbira kwa Abulahamu, Isaki ndi Yakobo kuti, ‘Ndidzapereka dziko ili kwa mbadwa* zako.’+ 2 Ndidzatumiza mngelo patsogolo panu+ ndipo ndidzathamangitsa Akanani, Aamori, Ahiti, Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi.+ 3 Mupite kudziko loyenda mkaka ndi uchi.+ Koma ine sindidzayenda pakati panu, chifukwa ndinu anthu okanika+ ndipo ndingakufafanizeni panjira.”+

4 Anthu atamva mawu odetsa nkhawa amenewa, anayamba kulira ndipo palibe aliyense amene anavala zodzikongoletsera. 5 Yehova anauza Mose kuti: “Uza Aisiraeli kuti, ‘Inu ndinu anthu okanika.+ Ndingathe kulowa pakati panu nʼkukufafanizani mʼkanthawi kochepa.+ Choncho musavale zodzikongoletsera pamene ndikuganizira zoti ndikuchiteni.’” 6 Choncho Aisiraeli sanavalenso* zodzikongoletsera kuyambira pamene anachoka paphiri la Horebe nʼkumapitiriza ulendo wawo.

7 Ndiyeno Mose anatenga tenti yake nʼkukaimanga kunja kwa msasa, chapatali ndi msasawo ndipo tentiyo anaipatsa dzina lakuti chihema chokumanako. Aliyense amene ankafuna kufunsa malangizo kwa Yehova+ ankapita kuchihema chokumanako chimene chinali kunja kwa msasa. 8 Ndiyeno Mose akamapita kuchihemako, munthu aliyense ankaimirira pakhomo la tenti yake nʼkumayangʼanitsitsa Mose mpaka atalowa mʼchihemacho. 9 Mose akangolowa mʼchihema, chipilala cha mtambo+ chinkatsika nʼkuima pakhomo la chihemacho pa nthawi imene Mulungu akulankhula ndi Mose.+ 10 Anthu onse akaona chipilala cha mtambo chitaima pakhomo la chihema, aliyense ankagwada pakhomo la tenti yake. 11 Yehova ankalankhula ndi Mose pamasomʼpamaso,+ mmene munthu amalankhulira ndi munthu mnzake. Mose akabwerera kumsasa, mtumiki wake Yoswa,+ mwana wa Nuni, sankachoka kuchihemako.

12 Tsopano Mose anauza Yehova kuti: “Inu mukundiuza kuti, ‘Tsogolera anthuwa,’ koma simunandidziwitse amene mudzamʼtume kuti ndipite naye. Komanso mwanena kuti, ‘Ndikukudziwa bwino ndi dzina lako lomwe,* ndipo ndakukomera mtima.’ 13 Ndiye ngati mwandikomeradi mtima, chonde ndidziwitseni njira zanu+ kuti ndikudziweni komanso kuti mupitirize kundikomera mtima. Kumbukiraninso kuti mtundu uwu ndi anthu anu.”+ 14 Choncho Mulungu anati: “Ineyo ndipita nawe+ ndipo ndidzakupatsa mpumulo.”+ 15 Kenako Mose anati: “Ngati inuyo simupita nafe, ndiye musatiuze kuti tichoke pano. 16 Ngati simupita nafe, kodi anthu adziwa bwanji kuti ine ndi anthu anuwa mwatikomera mtima? Koma mukapita nafe+ zisonyeza kuti ine ndi anthu anuwa mwatisiyanitsa ndi anthu ena onse amene ali padziko lapansi.”+

17 Yehova anapitiriza kuuza Mose kuti: “Ndichitanso zimene wapemphazi, chifukwa ndakukomera mtima ndipo ndikukudziwa bwino, ndi dzina lako lomwe.” 18 Kenako Mose anati: “Chonde ndionetseni ulemerero wanu.” 19 Koma Mulungu anati: “Ineyo ndidzakuonetsa ubwino wanga wonse, ndipo ndidzalengeza dzina langa lakuti Yehova kwa iwe.+ Amene ndikufuna kumukomera mtima ndidzamukomera mtima, ndipo amene ndikufuna kumusonyeza chifundo, ndidzamusonyeza chifundo.”+ 20 Ndiyeno anawonjezera kuti: “Sungathe kuona nkhope yanga, chifukwa palibe munthu amene angandione nʼkukhalabe ndi moyo.”

21 Yehova ananenanso kuti: “Pali malo pafupi ndi ine, ndipo ukaime pathanthwe. 22 Ulemerero wanga ukamadzadutsa pafupi ndi iwe, ndidzakuika kuphanga la thanthwelo, ndipo ndidzakuphimba ndi dzanja langa mpaka nditadutsa. 23 Kenako ndidzachotsa dzanja langa, ndipo udzaona msana wanga, koma nkhope yanga sungaione.”+

34 Kenako Yehova anauza Mose kuti: “Sema miyala iwiri yofanana ndi yoyamba ija,+ ndipo ine ndidzalemba pamiyala yosemayo mawu amene anali pamiyala yoyamba ija,+ imene iwe unaswa.+ 2 Ndipo ukonzeke kuti mawa mʼmawa ukakwere phiri la Sinai nʼkukakhala pamaso panga kumeneko pamwamba pa phirilo.+ 3 Koma usakwere mʼphirimo ndi wina aliyense, ndipo musapezeke wina aliyense mmenemo. Ngakhale nkhosa kapena ngʼombe zisadye mʼmunsi mwa phirilo.”+

4 Choncho Mose anasema miyala iwiri yofanana ndi yoyamba ija, ndipo anadzuka mʼmamawa kwambiri nʼkukwera phiri la Sinai atanyamula miyala iwiriyo mʼmanja mwake, mogwirizana ndi zimene Yehova anamulamula. 5 Kenako Yehova anatsika+ mumtambo nʼkuima pafupi ndi Mose ndipo analengeza dzina lake lakuti Yehova.+ 6 Ndiyeno Yehova anadutsa pamaso pa Mose akulengeza kuti: “Yehova, Yehova, Mulungu wachifundo+ ndi wokoma mtima,*+ wosakwiya msanga+ ndiponso wachikondi chokhulupirika chochuluka+ komanso choonadi.*+ 7 Amasonyeza chikondi chokhulupirika kwa mibadwo masauzande,+ amakhululuka zolakwa ndi machimo,+ koma sadzalekerera wolakwa osamʼpatsa chilango.+ Amalanga ana, zidzukulu ndi ana a zidzukuluzo chifukwa cha zolakwa za abambo awo.”+

8 Nthawi yomweyo Mose anagwada nʼkuweramira pansi. 9 Kenako iye anati: “Tsopano ngati mwandikomera mtima, inu Yehova, chonde Yehova, muyende nafe ndipo mukhale pakati pathu,+ ngakhale kuti ndife anthu ouma khosi.+ Mutikhululukirenso zolakwa zathu ndi machimo athu,+ ndipo mutitenge kukhala chuma chanu.” 10 Poyankha Mulungu anati: “Ine ndikuchita nanu pangano ili: Ndidzachita zinthu zodabwitsa pamaso pa anthu ako onse, zimene sizinachitikepo padziko lonse lapansi kapena pakati pa mitundu yonse.+ Ndipo anthu onse okuzungulirani adzaonadi ntchito za Yehova, chifukwa ndidzakuchitirani chinthu chochititsa mantha.+

11 Koma inu mumvere mosamala zimene ndikukulamulani lero.+ Inetu ndikuthamangitsa pamaso panu Aamori, Akanani, Ahiti, Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi.+ 12 Samalani kuti musachite pangano ndi anthu amʼdziko limene mukupitako,+ kuopera kuti ungakhale msampha kwa inu.+ 13 Koma maguwa awo ansembe mukawagwetse, zipilala zawo zopatulika mukaziphwanye ndipo mizati* yawo yopatulika mukaidule.+ 14 Musagwadire mulungu wina,+ chifukwa Yehova amafuna kuti anthu azidzipereka kwa iye yekha.* Iye ndi Mulungu amene amafuna kuti anthu azidzipereka kwa iye yekha.*+ 15 Samalani kuti musachite pangano ndi anthu okhala mʼdzikomo, chifukwa akamachita uhule ndi milungu yawo komanso kupereka nsembe kwa milungu yawo,+ wina adzakuitanani kunyumba kwake ndipo nanunso mudzadya nsembe yakeyo.+ 16 Kenako mudzatengadi ena mwa ana awo aakazi kuti akhale akazi a ana anu aamuna.+ Ndipo ana awo aakazi adzachita uhule ndi milungu yawo nʼkuchititsa ana anu aamuna kuchita uhule ndi milungu yawo.+

17 Musapange milungu ya chitsulo chosungunula.+

18 Muzichita Chikondwerero cha Mikate Yopanda Zofufumitsa.+ Mogwirizana ndi zimene ndinakulamulani, muzidya mikate yopanda zofufumitsa masiku 7 mʼmwezi wa Abibu* pa nthawi imene inaikidwa,+ chifukwa munatuluka mu Iguputo mʼmwezi wa Abibu.

19 Mwana aliyense wamwamuna woyamba kubadwa* ndi wanga,+ kuphatikizapo mwana woyamba kubadwa wa ziweto zanu zonse, kaya ndi mwana woyamba kubadwa wa ngʼombe kapena nkhosa.+ 20 Mwana woyamba kubadwa wa bulu muzimuwombola ndi nkhosa. Koma ngati simungamuwombole, muzimuthyola khosi. Ndipo muziwombola mwana wanu wamwamuna aliyense woyamba kubadwa.+ Palibe amene ayenera kuonekera kwa ine chimanjamanja.

21 Muzigwira ntchito zanu kwa masiku 6, koma pa tsiku la 7 muzipuma.*+ Ngakhale pa nthawi yolima ndi yokolola muzipuma.

22 Muzichita Chikondwerero cha Masabata,* ndipo pochita chikondwerero chimenechi muzipereka tirigu woyamba kucha pa tirigu amene mwakolola. Kumapeto kwa chaka muzichita Chikondwerero cha Zokolola.*+

23 Katatu pa chaka, mwamuna aliyense pakati panu azikaonekera pamaso pa Ambuye woona, Yehova, Mulungu wa Isiraeli.+ 24 Mitundu ya anthu ndidzaithamangitsira kutali ndi inu,+ ndipo ndidzakulitsa dera lanu. Palibe aliyense amene adzasirire dziko lanu mukapita kukaona nkhope ya Yehova Mulungu wanu katatu pa chaka.

25 Mukamapereka magazi a nsembe yanga musawapereke limodzi ndi chilichonse chokhala ndi zofufumitsa.+ Musamasunge nsembe ya chikondwerero cha Pasika mpaka mʼmawa.+

26 Zipatso zoyamba kucha zabwino kwambiri zamʼmunda mwanu muzibwera nazo kunyumba ya Yehova Mulungu wanu.+

Musamawiritse mwana wa mbuzi mumkaka wa mayi ake.”+

27 Yehova anapitiriza kuuza Mose kuti: “Ulembe mawuwa+ chifukwa ine ndikuchita pangano ndi iwe komanso Isiraeli mogwirizana ndi mawu amenewa.”+ 28 Choncho Mose anakhalabe mʼphirimo ndi Yehova masiku 40, masana ndi usiku. Iye sanadye mkate kapena kumwa madzi.+ Ndipo Mulungu analemba mawu a pangano, Malamulo Khumi,* pamiyala yosemayo.+

29 Ndiyeno Mose anatsika mʼphiri la Sinai atanyamula miyala iwiri ya Umboni ija mʼmanja mwake.+ Pamene ankatsika mʼphirimo, Mose sankadziwa kuti nkhope yake ikuwala chifukwa choti amalankhula ndi Mulungu. 30 Aroni ndi Aisiraeli onse ataona Mose, anaona kuti nkhope yake ikuwala ndipo anaopa kumuyandikira.+

31 Koma Mose anawaitana. Choncho Aroni ndi atsogoleri onse a gulu la Isiraeli anapita kwa iye, ndipo Mose analankhula nawo. 32 Kenako Aisiraeli onse anamuyandikira, ndipo iye anawapatsa malamulo onse amene Yehova anamupatsa mʼphiri la Sinai.+ 33 Mose akamaliza kulankhula nawo ankaika chophimba pankhope yake.+ 34 Koma Mose akamalowa mʼchihema chokumanako kukaonekera kwa Yehova kuti akalankhule naye, ankachotsa chophimbacho mpaka atatulukamo.+ Kenako ankapita kwa Aisiraeli nʼkuwauza zimene walamulidwa.+ 35 Ndipo Aisiraeli anaona kuti nkhope ya Mose ikuwala. Choncho Mose anaphimbanso nkhope yake mpaka atabwerera kukalankhula ndi Mulungu.+

35 Kenako Mose anaitana gulu lonse la Aisiraeli nʼkuwauza kuti: “Yehova walamula kuti tizichita zinthu izi:+ 2 Muzigwira ntchito masiku 6, koma tsiku la 7 likhale lopatulika kwa inu, likhale sabata la Yehova lopuma pa ntchito zanu zonse.+ Aliyense wogwira ntchito pa tsikuli adzaphedwa.+ 3 Pa tsiku la Sabata, musamayatse moto mʼmalo anu alionse amene mukukhala.”

4 Ndiyeno Mose anauza gulu lonse la Aisiraeli kuti: “Yehova walamula kuti, 5 ‘Nonse mupereke zopereka kwa Yehova.+ Aliyense amene ali ndi mtima wofunitsitsa+ apereke kwa Yehova zinthu monga golide, siliva, kopa,* 6 ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wapepo, ulusi wofiira kwambiri, nsalu zabwino kwambiri ndi ubweya wa mbuzi.+ 7 Aperekenso zikopa za nkhosa zonyika mu utoto wofiira, zikopa za akatumbu,* matabwa a mthethe, 8 mafuta a nyale, basamu wopangira mafuta odzozera ndi zofukiza zonunkhira,+ 9 miyala ya onekisi ndi miyala ina yoika pa efodi+ komanso pachovala pachifuwa.+

10 Anthu onse aluso*+ pakati panu abwere ndipo adzapange zinthu zonse zimene Yehova walamula. 11 Adzapange chihema ndi nsalu yoyala pachihemacho, chophimba chake, ngowe zake, mafelemu ake, ndodo zake, zipilala zake ndi zitsulo zake zokhazikapo mafelemu ndi zipilala. 12 Apangenso Likasa+ ndi ndodo zake zonyamulira,+ chivundikiro,+ katani,+ 13 tebulo+ ndi zipangizo zake zonse ndi ndodo zake zonyamulira, mkate wachionetsero,+ 14 choikapo nyale+ zounikira komanso zipangizo zake ndiponso nyale zake ndi mafuta a nyalezo.+ 15 Apangenso guwa lansembe zofukiza+ ndi ndodo zake zonyamulira, mafuta odzozera ndi zofukiza zonunkhira,+ nsalu yotchinga pakhomo la chihema, 16 guwa lansembe zopsereza+ ndi sefa wake wa zitsulo zakopa, ndodo zake zonyamulira ndi zipangizo zake zonse komanso beseni ndi choikapo chake.+ 17 Apange nsalu za mpanda wa bwalo,+ zipilala zake ndi zitsulo zake zokhazikapo zipilalazo, nsalu yotchinga pakhomo la bwalolo, 18 zikhomo za chihema, zikhomo za bwalo ndi zingwe zake.+ 19 Apangenso zovala zolukidwa bwino+ zoti azivala potumikira mʼmalo opatulika, zovala zopatulika za Aroni+ wansembe ndi zovala za ana ake zoti azivala potumikira monga ansembe.’”

20 Choncho gulu lonse la Aisiraeli linachoka pamaso pa Mose. 21 Kenako aliyense amene anali ndi mtima wofunitsitsa,+ komanso aliyense amene anali ndi mzimu wofunitsitsa, anabwera ndipo anabweretsa zopereka kwa Yehova zoti zikagwire ntchito pachihema chokumanako ndi pa utumiki wonse wochitika pamenepo. Anabweretsanso zinthu zopangira zovala zopatulika. 22 Iwo anapitiriza kubwera, amuna pamodzi ndi akazi, aliyense amene anali ndi mtima wofunitsitsa. Anabweretsa zokongoletsera zomanga pazovala, ndolo, mphete ndi zokongoletsera zina komanso zinthu zosiyanasiyana zagolide. Onse anapereka zopereka zawo zagolide* kwa Yehova.+ 23 Ndipo onse amene anali ndi ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wapepo, ulusi wofiira kwambiri, nsalu zabwino kwambiri, ubweya wa mbuzi, zikopa za nkhosa zonyika mu utoto wofiira ndi zikopa za akatumbu, anabwera nazo. 24 Onse amene anapereka chopereka chasiliva ndi kopa anapereka zoperekazo kwa Yehova, ndipo onse amene anali ndi matabwa a mthethe oti akagwire ntchito pa utumiki wonse wapachihema anabwera nawo.

25 Akazi onse aluso+ anawomba nsalu ndi manja awo, ndipo ankabweretsa zingwe zopota za ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wapepo, ulusi wofiira kwambiri ndi nsalu zabwino kwambiri. 26 Ndipo akazi onse aluso amene anali ndi mtima wofunitsitsa anawomba nsalu za ubweya wa mbuzi.

27 Atsogoleri anabweretsa miyala ya onekisi komanso miyala ina yoika pa efodi ndi pachovala pachifuwa,+ 28 mafuta a nyale, basamu wopangira mafuta odzozera+ ndi zofukiza zonunkhira.+ 29 Amuna ndi akazi onse amene anali ndi mtima wofunitsitsa anapereka kenakake kuti kathandize pa ntchito imene Yehova analamula kudzera mwa Mose. Aisiraeli anabweretsa zinthu zimenezi ngati nsembe yaufulu kwa Yehova.+

30 Kenako Mose anauza Aisiraeli kuti: “Yehova wasankha Bezaleli, mwana wamwamuna wa Uri, mwana wa Hura wa fuko la Yuda.+ 31 Ndipo wamupatsa mzimu wa Mulungu kuti akhale wanzeru, wozindikira komanso wodziwa kupanga zinthu mwaluso pa ntchito iliyonse. 32 Wodziwa kupanga mapulani a mmene angapangire zinthu mwaluso, kupanga zinthu zagolide, zasiliva ndi zakopa, 33 waluso losema miyala ndiponso kupanga zoikamo miyala komanso wodziwa kupanga mwaluso chilichonse chamatabwa. 34 Mulungu waika luso lophunzitsa mumtima mwa Bezaleli komanso mwa Oholiabu+ mwana wamwamuna wa Ahisama wa fuko la Dani. 35 Iye wawapatsa luso*+ kuti agwire ntchito zonse. Wawapatsa luso lopeta nsalu komanso luso loluka nsalu ndi ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wapepo, ulusi wofiira kwambiri, nsalu zabwino kwambiri ndi luso lowomba nsalu. Amuna amenewa adzagwira ntchito iliyonse komanso kukonza kapangidwe ka zinthu zosiyanasiyana.”

36 “Bezaleli adzagwire ntchito limodzi ndi Oholiabu komanso mwamuna aliyense waluso* amene Yehova wamupatsa nzeru ndi kuzindikira kuti adziwe mmene angagwirire ntchito zonse zopatulika mogwirizana ndi zimene Yehova walamula.”+

2 Kenako Mose anaitana Bezaleli, Oholiabu ndi mwamuna aliyense waluso amene Yehova anaika nzeru mumtima mwake.+ Anaitana aliyense amene anadzipereka mofunitsitsa kugwira ntchitoyo.+ 3 Ndipo iwo anatenga kwa Mose zopereka zonse+ zimene Aisiraeli anabweretsa kuti azigwiritse ntchito pa utumiki wopatulika. Koma Aisiraeliwo anapitirizabe kubweretsa kwa Mose nsembe zaufulu mʼmawa uliwonse.

4 Ndiye ntchito yopatulika itayambika, anthu onse aluso anayamba kubwera mmodzimmodzi. 5 Iwo ankauza Mose kuti: “Anthu akubweretsa zinthu zambiri kuposa zimene zikufunikira pa ntchito imene Yehova walamula kuti ichitike.” 6 Choncho Mose analamula kuti alengeze mumsasa wonsewo, kuti: “Amayi ndi abambo, musabweretsenso zinthu zina kuti chikhale chopereka chopatulika.” Ndi mawu amenewa anthuwo anasiya kubweretsa zinthuzo. 7 Zinthuzo zinali zokwanira pa ntchito yonse imene ankafuna kuti ichitike ndipo zinali zambiri kuposa zimene zinkafunika.

8 Choncho anthu onse aluso+ anapanga chihema.+ Anachipanga ndi nsalu 10 zopangira tenti zopangidwa ndi ulusi wopota wabwino kwambiri, ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wapepo ndi ulusi wofiira kwambiri. Iye* anapeta akerubi pa nsaluzo.+ 9 Nsalu iliyonse inali mamita 13* mulitali ndipo mulifupi inali mamita awiri. Nsalu zonse muyezo wake unali wofanana. 10 Kenako analumikiza nsalu 5 pamodzi ndipo analumikizanso nsalu zina 5 zija pamodzi. 11 Atatero anapanga zingwe zopota zabuluu zokolekamo ngowe mʼmphepete mwa nsalu imodzi pamene nsalu ziwirizo zidzalumikizane. Anachitanso chimodzimodzi mʼmphepete mwa nsalu yakumapeto kwenikweni, pamene nsaluzo zidzalumikizane. 12 Anaika zingwe zopota 50 zokolekamo ngowe pansalu imodzi, ndipo anaikanso zingwe zopota 50 zokolekamo ngowe mʼmphepete mwa nsalu inayo kuti zikhale moyangʼanizana pamalo olumikizirana. 13 Pomaliza anapanga ngowe 50 zagolide nʼkulumikiza nsalu za tenti ndi ngowezo moti nsaluzo zinakhala chinsalu chimodzi chopangira chihema.

14 Ndiyeno anapanga nsalu za ubweya wa mbuzi zoyala pachihema. Anapanga nsalu 11.+ 15 Nsalu iliyonse inali mamita 13 mulitali ndipo mulifupi inali mamita awiri. Nsalu zonse 11 muyezo wake unali wofanana. 16 Kenako analumikiza nsalu 5 pamodzi komanso analumikiza nsalu zina 6 pamodzi. 17 Atatero anaika zingwe zopota 50 zokolekamo ngowe mʼmphepete mwa nsalu yakumapeto kwenikweni, polumikizirana nsalu ziwirizi. Anaikanso zingwe zopota 50 zokolekamo ngowe mʼmphepete mwa nsalu inayo, pamalo amene nsalu ziwirizi zinalumikizana. 18 Atatero anapanga ngowe 50 zakopa zolumikizira nsaluzo kuti zikhale chinsalu chimodzi.

19 Anapanga chophimba chihemacho cha zikopa za nkhosa zonyika mu utoto wofiira ndi chophimba chinanso pamwamba pake cha zikopa za akatumbu.+

20 Kenako anapanga mafelemu oimika+ a chihema amatabwa a mthethe.+ 21 Felemu lililonse linali mamita 4 mulitali ndipo mulifupi linali masentimita 70. 22 Felemu lililonse linali ndi zolumikizira ziwiri zoyandikana. Mafelemu onse a chihema anawapanga choncho. 23 Iwo anapanga mafelemu 20 a mbali yakumʼmwera ya chihemacho. 24 Kenako anapanga zitsulo 40 zasiliva zokhazikapo mafelemu 20 aja. Zitsulo ziwiri anaziika pansi pa felemu lililonse ndipo munalowa zolumikizira ziwiri.+ 25 Kumbali ina ya chihemacho, mbali yakumpoto anaikako mafelemu 20, 26 ndi zitsulo zake 40 zasiliva zokhazikapo mafelemuwo. Zitsulo ziwiri zinali pansi pa felemu lililonse.

27 Anapanga mafelemu 6 nʼkuwaika kumbuyo kwa chihemacho, mbali yakumadzulo.+ 28 Anapanga mafelemu awiri kuti akhale ochirikiza mʼmakona awiri akumbuyo kwa chihemacho. 29 Mafelemu amenewo anali ndi matabwa awiri ophatikiza kuyambira pansi mpaka pamwamba, pamene pali mphete yoyamba. Izi nʼzimene anachita ndi mafelemu onse ochirikiza mʼmakona. 30 Choncho anapanga mafelemu 8 ndi zitsulo 16 zasiliva zokhazikapo mafelemuwo. Zitsulo ziwiri zinali pansi pa felemu lililonse.

31 Ndiyeno anapanga ndodo zamtengo wa mthethe, ndodo 5 za mafelemu a mbali imodzi ya chihema,+ 32 ndi ndodo zinanso 5 za mafelemu a mbali ina ya chihema. Anapanganso ndodo zina 5 za mafelemu akumbuyo kwa chihema, mbali yakumadzulo. 33 Kenako anapanga ndodo yodutsa pakati pa mafelemu onse kuchokera koyambirira mpaka kumapeto. 34 Ndiyeno anakuta mafelemuwo ndi golide ndipo anapanga mphete zake zagolide zolowetsamo ndodo. Ndodozo anazikuta ndi golide.+

35 Kenako anapanga katani+ ya ulusi wabuluu, ya ubweya wa nkhosa wapepo, ulusi wofiira kwambiri ndi ulusi wopota wabwino kwambiri. Pakataniyo anapetapo+ akerubi.+ 36 Ndiyeno katani imeneyi anaipangira zipilala 4 za mtengo wa mthethe ndipo anazikuta ndi golide. Anapanganso tizitsulo tagolide tokolowekapo katani komanso zitsulo 4 zasiliva zokhazikapo zipilalazo. 37 Atatero anawomba nsalu yotchinga khomo la chihema. Nsaluyo inali ya ulusi wabuluu, ya ubweya wa nkhosa wapepo, ulusi wofiira kwambiri ndi ulusi wopota wabwino kwambiri.+ 38 Anapanganso zipilala zake 5 ndi tizitsulo take tokolowekapo nsalu yotchingayo. Pamwamba pa zipilalazo anakutapo ndi golide komanso tizitsulo take tolumikizira anatikuta ndi golide. Koma zitsulo zake 5 zokhazikapo zipilalazo zinali zakopa.

37 Kenako Bezaleli+ anapanga Likasa+ la mtengo wa mthethe masentimita 110* mulitali, masentimita 70 mulifupi ndi masentimita 70 kuchoka pansi kupita mʼmwamba.+ 2 Analikuta ndi golide woyenga bwino mkati ndi kunja komwe ndipo anapanga mkombero wagolide kuzungulira Likasalo.+ 3 Ndiyeno analipangira mphete 4 zagolide zoika pamwamba pa miyendo yake 4. Mphete ziwiri zinali mbali imodzi ndipo mphete zina ziwiri zinali mbali inayo. 4 Anapanganso ndodo zonyamulira za mtengo wa mthethe ndipo anazikuta ndi golide.+ 5 Kenako analowetsa ndodo zonyamulirazo mumphete zamʼmbali mwa Likasa zija kuti azinyamulira Likasalo.+

6 Anapanga chivundikiro chagolide woyenga bwino+ masentimita 110 mulitali ndi masentimita 70 mulifupi.+ 7 Anapanganso akerubi awiri+ agolide. Anali osula ndipo anawaika kumapeto onse awiri a chivundikirocho.+ 8 Kerubi mmodzi anamuika kumbali imodzi ya chivundikirocho ndipo kerubi wina anamuika kumbali inayo. Akerubiwo anawapanga kumapeto onse awiri a chivundikirocho. 9 Mapiko a akerubi awiriwo anawakweza mʼmwamba nʼkuwatambasula ndipo anaphimba chivundikirocho ndi mapiko awo.+ Akerubiwo anakhala moyangʼanizana ndipo nkhope zawo zinaweramira pachivundikirocho.+

10 Ndiyeno anapanga tebulo la mtengo wa mthethe+ masentimita 90 mulitali, masentimita 45 mulifupi ndi masentimita 70 kuchoka pansi mpaka mʼmwamba.+ 11 Analikuta ndi golide woyenga bwino ndipo anapanga mkombero wagolide kuzungulira tebulo lonselo. 12 Analipangiranso felemu kuzungulira tebulo lonse muyezo wake masentimita 7* mulifupi mwake ndipo anapanga mkombero wagolide pafelemulo. 13 Kuwonjezera pamenepo, analipangira mphete 4 zagolide nʼkuziika mʼmakona ake 4 mmene munali miyendo yake 4. 14 Mphetezo zinali pafupi ndi felemu lija kuti muzilowa ndodo zonyamulira tebulolo. 15 Kenako anapanga ndodo zonyamulira za mtengo wa mthethe nʼkuzikuta ndi golide. Ndodo zimenezi zinali zonyamulira tebulolo. 16 Atatero anapanga ziwiya zapatebulolo, mbale zake, makapu, mitsuko ndi mbale zolowa zoti azithirira nsembe zachakumwa. Anazipanga ndi golide woyenga bwino.+

17 Kenako anapanga choikapo nyale+ chagolide woyenga bwino ndipo chinali chosula. Choikapo nyalecho chinali chinthu chimodzi ndipo chinali ndi tsinde, thunthu, timasamba tamʼmunsi mwa duwa, mphindi ndi maluwa.+ 18 Choikapo nyalecho chinali ndi nthambi 6. Kumbali ina kunali nthambi zitatu ndipo kumbali inayo kunalinso nthambi zitatu. 19 Panthambi za mbali imodzi, iliyonse inali ndi timasamba titatu tamʼmunsi mwa duwa topangidwa ngati maluwa a mtengo wa amondi ndipo timasambato tinatsatizana ndi mphindi ndi maluwa. Panthambi za mbali inayo, iliyonse inalinso ndi timasamba titatu tamʼmunsi mwa duwa topangidwa ngati maluwa a mtengo wa amondi, ndipo timasambato tinatsatizana ndi mphindi ndi maluwa. Nthambi 6 zotuluka muthunthu la choikapo nyalecho anazipanga choncho. 20 Pathunthu la choikapo nyalecho panali timasamba 4 tamʼmunsi mwa duwa topangidwa ngati maluwa a mtengo wa amondi, ndipo timasambato tinatsatizana ndi mphindi ndi maluwa. 21 Mphindi imodzi inali pansi pa nthambi zake ziwiri zoyambirira. Mphindi ina inalinso pansi pa nthambi zake ziwiri, ndipo mphindi inanso inali pansi pa nthambi zinanso ziwiri. Zinali choncho ndi nthambi 6 zotuluka muthunthu la choikapo nyale. 22 Choikapo nyale chonsecho kuphatikizapo mphindi ndi nthambi zake chinali chimodzi ndipo anachisula ndi golide woyenga bwino. 23 Kenako anachipangira nyale 7,+ zopanira zake zozimitsira nyale ndi mbale zake zoikamo phulusa la zingwe za nyale. Zonsezi zinali zagolide woyenga bwino. 24 Choikapo nyalecho pamodzi ndi ziwiya zake zonsezi anazipanga pogwiritsa ntchito golide woyenga bwino wolemera talente imodzi.*

25 Kenako anapanga guwa lansembe zofukiza+ la matabwa a mthethe. Mulitali mwake linali masentimita 45, mulifupi mwake masentimita 45. Mbali zake zonse 4 zinali zofanana, ndipo kutalika kwake kuchoka pansi mpaka mʼmwamba linali masentimita 90. Nyanga zake anazipangira kumodzi ndi guwalo.*+ 26 Analikuta ndi golide woyenga bwino pamwamba pake ndi mʼmbali mwake kuzungulira guwalo komanso nyanga zake. Ndipo anapanga mkombero wagolide kuzungulira guwa lonselo. 27 Anapanga mphete ziwiri zagolide mʼmunsi mwa mkombero kumbali zake ziwiri zoyangʼanizana kuti muzilowa ndodo zonyamulira guwalo. 28 Kenako anapanga ndodo zonyamulira za mtengo wa mthethe ndipo anazikuta ndi golide. 29 Anapanganso mafuta ogwiritsa ntchito pa kudzoza kopatulika+ ndi mafuta onunkhira abwino kwambiri,+ osakanizidwa mwaluso.*

38 Ndiyeno anapanga guwa lansembe zopsereza lamatabwa a mthethe. Guwalo linali lofanana muyezo wake mbali zake zonse 4, mulitali linali mamita awiri* ndipo mulifupi linalinso mamita awiri. Kutalika kwake kuchokera pansi mpaka mʼmwamba linali masentimita 134.+ 2 Anapanganso nyanga mʼmakona ake 4. Nyanga zake anazipangira kumodzi ndi guwalo.* Atatero anakuta guwalo ndi kopa.*+ 3 Kenako anapanga ziwiya zonse zogwiritsa ntchito paguwalo. Anapanga ndowa, mafosholo, mbale zolowa, mafoloko aakulu ndi zopalira moto. Ziwiya zake zonse anazipanga ndi kopa. 4 Guwalo analipangiranso sefa wa zitsulo zakopa. Analowetsa sefayo chapakati pa guwa lansembe, mʼmunsi mwa mkombero. 5 Analipangiranso mphete 4 mʼmakona ake 4 kuti muzilowa ndodo zonyamulira. Mphetezo anazilumikiza pafupi ndi sefa wa zitsulo zakopa. 6 Kenako anapanga ndodo zonyamulira za mtengo wa mthethe, ndipo anazikuta ndi kopa. 7 Ndodozo anazilowetsa mumphetezo mʼmbali mwa guwa kuti zikhale zonyamulira guwalo. Guwa limenelo analipanga ngati bokosi lamatabwa losatseka pansi.

8 Kenako anapanga beseni losambira lakopa+ ndi choikapo chake chakopa. Popanga zimenezi anagwiritsa ntchito magalasi odziyangʼanira* a azimayi amene ankatumikira pakhomo la chihema chokumanako.

9 Ndiyeno anapanga bwalo.+ Kumbali yakumʼmwera ya bwalolo anapangako mpanda wa nsalu za ulusi wopota wabwino kwambiri. Mpandawo unali mamita 45 mulitali mwake.+ 10 Panali zipilala 20 ndi zitsulo 20 zakopa zokhazikapo zipilalazo. Tizitsulo ta zipilala tokolowekapo nsalu ndi tizitsulo tolumikizira tinali tasiliva. 11 Kumbali yakumpoto, mpandawo unali mamita 45 mulitali mwake. Zipilala zake 20 ndi zitsulo 20 zokhazikapo zipilalazo zinali zakopa. Tizitsulo ta zipilala tokolowekapo nsalu ndi tizitsulo tolumikizira tinali tasiliva. 12 Koma kumbali yakumadzulo, mpanda wa nsaluwo unali mamita 23 mulitali mwake. Kunali zipilala 10 ndi zitsulo 10 zokhazikapo zipilalazo. Tizitsulo ta zipilala tokolowekapo nsalu ndi tizitsulo tolumikizira tinali tasiliva. 13 Mulifupi mwake kumbali yakumʼmawa, kotulukira dzuwa, mpandawo unali mamita 23. 14 Kumbali imodzi ya khomo la bwalo, mpanda wa nsaluwo unali mamita 7. Kunali zipilala zitatu ndi zitsulo zitatu zokhazikapo zipilalazo. 15 Ndipo kumbali ina ya khomo la bwalolo, mpandawo unali mamita 7 mulitali mwake. Kunali zipilala zitatu ndi zitsulo zitatu zokhazikapo zipilalazo. 16 Nsalu zonse za mpanda wotchingira bwalo lonselo zinali za ulusi wopota wabwino kwambiri. 17 Zitsulo zokhazikapo zipilala zinali zakopa. Tizitsulo ta zipilala tokolowekapo nsalu za mpanda ndi tizitsulo tolumikizira tinali tasiliva. Pamwamba pa zipilalazo panali pokutidwa ndi siliva, ndipo zipilala zonse za bwalo zinali ndi tizitsulo tasiliva tolumikizira.+

18 Nsalu yotchinga pakhomo la bwalo anaiwomba ndi ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wapepo, ulusi wofiira kwambiri ndi ulusi wopota wabwino kwambiri. Inali mamita 9 mulitali mwake, ndipo kutalika kwake kuchokera pansi mpaka mʼmwamba inali mamita awiri, mofanana ndi nsalu zotchingira mpanda wa bwalo.+ 19 Zipilala zake 4 ndi zitsulo 4 zokhazikapo zipilalazo zinali zakopa. Tizitsulo ta zipilalazo tokolowekapo nsalu tinali tasiliva, ndipo pamwamba pa zipilalazo ndi tizitsulo tolumikizira anazikuta ndi siliva. 20 Zikhomo zonse za chihema ndi za bwalo lonse zinali zakopa.+

21 Mose analamula kuti awerengere zinthu zonse zimene anagwiritsa ntchito popanga chihema, kapena kuti chihema cha Umboni.+ Alevi ndi amene anachita zimenezi+ motsogoleredwa ndi Itamara+ mwana wa Aroni wansembe. 22 Bezaleli+ mwana wa Uri, mwana wa Hura wa fuko la Yuda, anachita zonse zimene Yehova analamula Mose. 23 Iye anali ndi Oholiabu,+ mwana wamwamuna wa Ahisama wa fuko la Dani, mmisiri wa ntchito zosiyanasiyana, katswiri wodziwa kupeta komanso wodziwa kuwomba nsalu ndi ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wapepo, ulusi wofiira kwambiri ndi nsalu zabwino kwambiri.

24 Golide yense amene anagwiritsidwa ntchito pa ntchito yonse yapamalo oyera, anali wochuluka mofanana ndi golide wa nsembe yoyendetsa uku ndi uku.+ Muyezo wake unali matalente* 29 ndi masekeli* 730 potengera muyezo wa sekeli lakumalo oyera.* 25 Ndipo siliva wa anthu amene anawerengedwa mʼgulu la Isiraeli, anali matalente 100 ndi masekeli 1,775 potengera muyezo wa sekeli lakumalo oyera.* 26 Mwamuna aliyense amene anawerengedwa, kuyambira wa zaka 20 kupita mʼtsogolo,+ anapereka hafu ya sekeli potengera muyezo wa sekeli lakumalo oyera.* Anthu onse amene anawerengedwa analipo 603,550.+

27 Popanga zitsulo za malo oyera zokhazikapo mafelemu ndi zitsulo zokhazikapo zipilala za makatani anagwiritsa ntchito matalente 100. Popanga zitsulo 100 anagwiritsa ntchito matalente 100, talente imodzi anapangira chitsulo chimodzi.+ 28 Masekeli 1,775 anawagwiritsa ntchito popangira tizitsulo ta zipilala tokolowekapo nsalu ndi kukutira pamwamba pa zipilalazo. Atatero analumikiza zipilalazo.

29 Kopa amene anthu anapereka* anali matalente 70 ndi masekeli 2,400. 30 Kopa ameneyu anamugwiritsa ntchito popanga zitsulo zokhazikapo zipilala zapakhomo la chihema chokumanako, guwa lansembe lakopa, sefa wazitsulo wa guwalo ndi ziwiya zonse zogwiritsa ntchito paguwalo. 31 Anapangiranso zitsulo zokhazikapo zipilala za mpanda wa bwalo lonse, zitsulo zokhazikapo zipilala zapakhomo la bwalolo, zikhomo zonse za chihema ndi zikhomo zonse za bwalo.+

39 Ndiyeno anapanga zovala zolukidwa bwino zoti azivala potumikira mʼmalo oyera. Zovalazo anazipanga pogwiritsa ntchito ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wapepo ndi ulusi wofiira kwambiri.+ Anapanga zovala zopatulika za Aroni+ mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose.

2 Anapanga efodi+ wopeta ndi golide, ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wapepo, ulusi wofiira kwambiri ndi ulusi wopota wabwino kwambiri. 3 Anasula golide kukhala wopyapyala kwambiri, ndipo anamulezaleza kukhala ngati tizingwe kuti apetere limodzi ndi ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wapepo, ulusi wofiira kwambiri ndi ulusi wabwino kwambiri. 4 Anapanganso nsalu ziwiri zamʼmapewa nʼkuzilumikiza ku efodiyo. Anazilumikiza kutsogolo ndi kumbuyo kwake. 5 Lamba* woluka womangira efodi amene anamulumikiza ku efodiyo+ anali wopangidwa ndi nsalu ya efodi yomweyo. Anali wagolide, ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wapepo, ulusi wofiira kwambiri ndi ulusi wopota wabwino kwambiri, mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose.

6 Ndiyeno anaika miyala ya onekisi mʼzoikamo zagolide. Pamiyalayo analembapo mayina a ana a Isiraeli mochita kugoba ngati mmene amagobera chidindo.+ 7 Ndipo miyalayo anailowetsa pansalu zamʼmapewa za efodi kuti ikhale miyala yachikumbutso kwa ana a Isiraeli,+ mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose. 8 Kenako anapanga chovala pachifuwa+ ndipo anachipanga mwaluso mofanana ndi efodi. Anachipanga ndi golide, ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wapepo, ulusi wofiira kwambiri ndi ulusi wopota wabwino kwambiri.+ 9 Akachipinda pakati chinali chofanana mbali zonse 4. Chovala pachifuwacho anachipanga kuti akachipinda pakati, mulitali mwake chizikhala masentimita 22* ndiponso mulifupi mwake masentimita 22. 10 Ndiyeno pachovala pachifuwacho anaikapo mizere 4 ya miyala. Mzere woyamba unali ndi miyala ya rube, topazi ndi emarodi. 11 Mzere wachiwiri unali ndi miyala ya nofeki, safiro ndi yasipi. 12 Mzere wachitatu unali ndi miyala ya lesemu,* agate ndi ametusito. 13 Ndipo mzere wa 4 unali ndi miyala ya kulusolito, onekisi ndi yade. Anaiika mʼzoikamo zake zagolide. 14 Miyalayo anaiika mogwirizana ndi mayina a ana 12 a Isiraeli. Mwala uliwonse analembapo mochita kugoba ngati mmene amagobera chidindo ndipo mwala uliwonse unali ndi dzina limodzi mwa mayina a mafuko 12.

15 Ndipo pachovala pachifuwa anapangapo matcheni agolide woyenga bwino, okhala ngati zingwe zopota.+ 16 Anapanganso zoikamo miyala ziwiri zagolide ndi mphete ziwiri zagolide, ndipo anaika mphete ziwirizo mʼmakona awiri a chovala pachifuwacho. 17 Kenako analowetsa zingwe ziwiri zagolide zija mumphete ziwiri zamʼmakona a chovala pachifuwa. 18 Ndipo analowetsa zingwe ziwirizo pa zoikamo miyala ziwiri. Kenako anaika zoikamo miyala ziwirizo pansalu zamʼmapewa za efodi chakutsogolo. 19 Atatero anapanga mphete ziwiri zagolide nʼkuziika mʼmakona awiri a chovala pachifuwa kumbali yamkati yokhudzana ndi efodi.+ 20 Ndiyeno anapanga mphete zina ziwiri zagolide nʼkuziika kutsogolo kwa efodi, mʼmunsi mwa nsalu ziwiri zamʼmapewa, pafupi ndi polumikizira, pamwamba pa malo amene lamba* woluka walumikizana ndi efodi. 21 Atatero anamanga chovala pachifuwacho ndi chingwe chabuluu. Chingwe chimenecho chinalowa mumphete za chovala pachifuwa komanso mphete za efodi. Zimenezi zinkathandiza kuti chovala pachifuwacho chisamasunthe koma chizikhala pamwamba pa lamba* woluka wa efodi, mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose.

22 Ndiyeno anapanga malaya odula manja ovala mkati mwa efodi. Anapangidwa ndi woomba nsalu ndipo anawapanga ndi ulusi wabuluu wokhawokha.+ 23 Malaya odula manjawo anali otsegula pamwamba pake, pakatikati. Anali otsegula ngati chovala chakunkhondo cha mamba achitsulo. Potsegulapo panali popenderera mʼmphepete mwake kuti pasangʼambike. 24 Kenako, mumpendero wamʼmunsi wa malaya odula manjawo anapangamo zinthu zooneka ngati makangaza za ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wapepo ndi ulusi wofiira kwambiri wopota pamodzi. 25 Anapanganso mabelu agolide woyenga bwino nʼkuwaika pakati pa makangaza, kuzungulira mpendero wamʼmunsi wa malaya odula manjawo. 26 Anaika belu kenako khangaza,* belu kenako khangaza, kuzungulira mpendero wamʼmunsi mwa malaya odula manja. Malayawo ankavala potumikira, mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose.

27 Kenako anawomba nsalu ya ulusi wabwino kwambiri nʼkupangira mikanjo ya Aroni ndi ana ake.+ 28 Anapanganso nduwira+ ya nsalu yabwino kwambiri, mipango yokongola yokulunga kumutu+ ya nsalu zabwino kwambiri ndi makabudula a nsalu*+ za ulusi wopota wabwino kwambiri. 29 Anapanganso lamba wapamimba ndi ulusi wopota wabwino kwambiri, ulusi wabuluu, ubweya wa nkhosa wapepo ndi ulusi wofiira kwambiri, mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose.

30 Atatero anapanga kachitsulo konyezimira kagolide woyenga bwino, chizindikiro chopatulika cha kudzipereka. Analembapo mawu akuti: “Yehova ndi Woyera.” Mawuwa anawalemba mochita kugoba ngati mmene amagobera chidindo.+ 31 Analowetsa chingwe chopangidwa ndi ulusi wabuluu mʼkachitsuloko kuti akamangirire panduwirayo, mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose.

32 Choncho ntchito yonse ya chihema, kapena kuti chihema chokumanako, inatha ndipo Aisiraeli anachita zonse zimene Yehova analamula Mose.+ Anachitadi zomwezo.

33 Kenako anabweretsa kwa Mose chihema+ ndi zipangizo zake zonse, nsalu yake yophimba pamwamba,+ ngowe zake,+ mafelemu ake,+ ndodo zake+ zonyamulira, zipilala zake ndi zitsulo zoika pansi.+ 34 Anabweretsanso chophimba chihemacho cha zikopa za nkhosa zonyika mu utoto wofiira,+ chophimba chinanso chapamwamba pake cha chikopa cha akatumbu, katani,+ 35 likasa la Umboni, ndodo zake zonyamulira,+ chivundikiro chake,+ 36 tebulo, ziwiya zake zonse+ ndi mkate wachionetsero. 37 Anabweretsanso choikapo nyale chagolide woyenga bwino, nyale zake+ zondandalikidwa bwino, ziwiya zonse za choikapo nyalecho,+ mafuta a nyale,+ 38 guwa lansembe+ lagolide, mafuta odzozera,+ zofukiza zonunkhira,+ nsalu yotchinga+ pakhomo la chihemacho, 39 guwa lansembe lakopa,+ sefa wake wa zitsulo zakopa, ndodo zake zonyamulira,+ ziwiya zonse+ zogwiritsa ntchito paguwalo, beseni losambira ndi choikapo chake.+ 40 Anabweretsanso nsalu zotchingira bwalo, zipilala ndi zitsulo zokhazikapo zipilalazo,+ nsalu yotchinga+ pakhomo la bwalo, zikhomo za bwalo ndi zingwe zake,+ ziwiya zonse zogwiritsa ntchito pa utumiki wapachihema, kapena kuti chihema chokumanako, 41 zovala zolukidwa bwino zoti azivala potumikira mʼmalo opatulika, zovala zopatulika za Aroni wansembe+ ndi zovala za ana ake zoti azivala potumikira monga ansembe.

42 Aisiraeli anagwira ntchito yonse motsatira zonse zimene Yehova analamula Mose.+ 43 Mose atayendera ntchito yonse, anaona kuti achita zonse mogwirizana ndi zimene Yehova analamula, ndipo Mose anawadalitsa.

40 Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti: 2 “Pa tsiku loyamba la mwezi woyamba, udzamange chihema kapena kuti chihema chokumanako.+ 3 Mkati mwake udzaikemo likasa la Umboni+ ndipo udzatchinge kumene kuli Likasalo ndi katani.+ 4 Mʼchihemacho udzaikemonso tebulo+ ndipo udzaikepo zinthu zake mwadongosolo. Kenako udzaikemo choikapo nyale+ nʼkuyatsa nyale zake.+ 5 Ndiyeno udzaike guwa lansembe zofukiza lagolide+ patsogolo pa likasa la Umboni, nʼkuika nsalu yotchinga pakhomo la chihema.+

6 Udzaike guwa lansembe zopsereza+ patsogolo pa khomo la chihema kapena kuti chihema chokumanako. 7 Ndipo udzaike beseni pakati pa chihema chokumanako ndi guwa lansembe nʼkuthiramo madzi.+ 8 Kenako udzatchinge bwalo la chihema+ ndi mpanda ndipo pakhomo pa bwalolo udzaikepo nsalu yake yotchinga.+ 9 Kenako udzatenge mafuta odzozera+ nʼkudzoza chihema ndi zonse zimene zili mkati mwake+ ndipo udzachiyeretse pamodzi ndi ziwiya zake zonse kuti chikhale chopatulika. 10 Udzadzozenso guwa lansembe zopsereza ndi ziwiya zake zonse nʼkuliyeretsa, kuti guwalo lidzakhale lopatulika kwambiri.+ 11 Ndiponso udzadzoze beseni ndi choikapo chake nʼkuliyeretsa.

12 Kenako udzabweretse Aroni ndi ana ake pafupi ndi khomo la chihema chokumanako ndipo udzawasambitse ndi madzi.+ 13 Ukatero udzaveke Aroni zovala zopatulika+ kenako nʼkumudzoza+ komanso kumuyeretsa ndipo adzatumikira monga wansembe wanga. 14 Kenako udzatenge ana ake nʼkuwaveka mikanjo.+ 15 Udzawadzoze ngati mmene unadzozera bambo awo+ kuti atumikire monga ansembe anga. Iwo akadzadzozedwa adzapitiriza kutumikira monga ansembe mʼmibadwo yawo yonse.”+

16 Mose anachita zonse mogwirizana ndi zimene Yehova anamulamula.+ Anachitadi zomwezo.

17 Choncho mʼmwezi woyamba wa chaka chachiwiri, pa tsiku loyamba la mweziwo, anamanga chihema.+ 18 Pamene Mose ankamanga chihemacho, anayala pansi zitsulo zake+ nʼkukhazikamo mafelemu.+ Ndiyeno analowetsa ndodo zake+ nʼkuimika zipilala pamalo ake. 19 Atatero anayala nsalu+ yophimba pachihemacho ndi inanso yophimba+ pamwamba pake, mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose.

20 Kenako anatenga Umboni+ ndi kuuika mu Likasa,+ ndipo analowetsa ndodo zonyamulira+ mʼmbali mwa Likasalo nʼkuika chivundikiro+ pamwamba pa Likasa.+ 21 Atatero analowetsa Likasa mʼchihema nʼkuika katani+ pamalo ake ndipo inatchinga likasa la Umboni,+ mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose.

22 Ndiyeno analowetsa tebulo+ mʼchihema chokumanako nʼkuliika kumbali yakumpoto ya chihemacho, kunja kwa katani. 23 Kenako anaika mkate+ pamalo ake pamaso pa Yehova, mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose.

24 Anaika choikapo nyale+ mʼchihema chokumanako patsogolo pa tebulo, kumbali yakumʼmwera ya chihemacho. 25 Ndipo anayatsa nyalezo+ pamaso pa Yehova, mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose.

26 Kenako anaika guwa lansembe lagolide+ mʼchihema chokumanako patsogolo pa katani, 27 kuti azifukizirapo zofukiza+ zonunkhira,+ mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose.

28 Atatero anaika nsalu yotchinga+ pakhomo la chihema.

29 Ndiyeno anaika guwa lansembe zopsereza+ pakhomo la chihema kapena kuti chihema chokumanako, kuti aziperekerapo nsembe yopsereza+ ndi nsembe yambewu, mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose.

30 Kenako anaika beseni pakati pa chihema chokumanako ndi guwa lansembe nʼkuthiramo madzi osamba.+ 31 Mose, Aroni ndi ana ake ankasamba mʼmanja ndi mapazi awo pamenepo. 32 Akamalowa mʼchihema chokumanako ndiponso akamapita kuguwa lansembe ankasamba,+ mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose.

33 Pomaliza anamanga mpanda kuzungulira bwalo+ la chihema ndi guwa lansembe ndipo anaika nsalu yotchinga pakhomo la bwalolo.+

Choncho Mose anamaliza ntchitoyo. 34 Kenako mtambo unayamba kuphimba chihema chokumanako ndipo ulemerero wa Yehova unadzaza mʼchihemacho.+ 35 Mose sanathenso kulowa mʼchihema chokumanako, chifukwa mtambo unali utaphimba chihemacho ndipo munadzaza ulemerero wa Yehova.+

36 Mʼzigawo zonse za ulendo wawo, mtambowo ukachoka pamwamba pa chihemacho nʼkukwera mʼmwamba, Aisiraeli ankanyamuka nʼkuyamba ulendo.+ 37 Koma ukapanda kukwera mʼmwamba, iwo sankanyamuka mpaka tsiku limene udzakwere.+ 38 Mtambo wa Yehova unkakhala pamwamba pa chihema masana ndipo usiku pankakhala moto. Nyumba yonse ya Isiraeli inkaona zimenezi mʼzigawo zonse za ulendo wawo.+

Mʼchilankhulo choyambirira, “amene anatuluka pantchafu ya Yakobo.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Ana a Isiraeli.”

Mʼmizinda imeneyi anamangamo nkhokwe ndi nyumba zina zosungiramo chakudya ndi zinthu zina.

“Mzamba” ndi munthu amene amathandiza amayi pobereka. Ena amamutcha “namwino.”

Kapena kuti, “kabokosi.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Kutanthauza, “Wovuulidwa,” kapena kuti, wopulumutsidwa mʼmadzi.

Kapena kuti, “Mose atayamba kukhala wamphamvu.”

Kapena kuti, “nʼkuteteza.”

Reueli amatchedwanso kuti Yetero.

Kutanthauza, “Mlendo Kumeneko.”

Yetero amatchedwanso kuti Reueli.

Mʼchilankhulo choyambirira, “bambo.”

Kapena kuti, “mudzalambira.”

Kapena kuti, “Ndidzakhala Amene Ndidzasankhe Kukhala.” Onani Zakumapeto A4.

Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼkamwa mwanga ndi molemera.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “ndi pakamwa pako.”

Kapena kuti, “ankafunafuna moyo wako.”

Kapena kuti, “mpeni wamwala.”

Kapena kuti, “nʼkumupsompsona.”

Kapena kuti, “ku ukapolo wanu.”

Kapena kuti, “chifukwa mwatinunkhitsa kwa Farao ndi atumiki ake.”

Kapena kuti, “lamphamvu.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “ndinalumbira nditakweza dzanja langa.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “ndili ndi milomo yosadulidwa.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mogwirizana ndi magulu awo ankhondo.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “ndili ndi milomo yosadulidwa.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “ndakupanga kukhala Mulungu.”

Zimenezi ndi ngalande zochokera mumtsinje wa Nailo.

Timeneti ndi tizilombo tingʼonotingʼono ta ku Iguputo timene timaluma ngati udzudzu.

Amenewa ndi Aiguputo.

Ena amati “mahosi.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mwaye.”

Mwina akufotokoza za mphezi yamphamvu.

“Fulakesi” ndi mbewu imene inkalimidwa ku Iguputo. Ankaigwiritsa ntchito popanga ulusi wowombera nsalu.

Mʼchilankhulo choyambirira, “tirigu ndi sipeloti.” Sipeloti ndi mtundu wa tirigu koma wosakoma ngati tirigu weniweni. Anthu a ku Iguputo kalekalelo ankalima mbewuyi.

Kapena kuti, “chifukwa amadzalidwa mochedwa.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “apitiriza kukhala msampha kwa ife.”

Kapena kuti, “mutilole kutenga.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “chiboda.”

“Mphero” ndi mwala umene ankaugwiritsa ntchito popera mbewu kuti apange ufa.

Mʼchilankhulo choyambirira, “pakati pa madzulo awiri.” Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Pasika amatanthauza “kulumpha,” kapena “kupitirira.” Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Amenewa ndi ana a nkhosa kapena mbuzi.

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Kapena kuti, “Anaunyamulira mʼmbale.”

Amenewa ndi anthu osiyanasiyana omwe sanali Aisiraeli ndipo ena mwa anthu amenewa anali Aiguputo.

Mʼchilankhulo choyambirira, “Ndiyeno kukhala kwa ana a Isiraeli, amene anakhala mʼdziko la Iguputo.” Mabaibulo ena akale amasonyeza kuti chiwerengero cha zaka chimene chatchulidwachi sichikuimira zaka zimene Aisiraeli anakhala mu Iguputo mokha ayi, komanso chikuphatikizapo zaka zimene anakhala ku Kanani.

Kutanthauza kuti, “Munthu amene si wa Chiisiraeli.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “ana a Isiraeli limodzi ndi makamu awo.”

Kapena kuti, “Muyeretse.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mwana aliyense woyamba kubadwa, wotsegula mimba ya mayi aliyense.”

Onani Zakumapeto B15.

Mʼchilankhulo choyambirira, “pakati pa maso anu.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “aliyense wotsegula mimba ya mayi ake.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “iliyonse yotsegula mimba ya mayi ake.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “pakati pa maso anu.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Mʼchilankhulo choyambirira, “ndi dzanja limene lakwezedwa.”

Kutanthauza cha mʼma 2 koloko usiku mpaka 6 koloko mʼmawa.

Mʼchilankhulo choyambirira, “dzanja.”

Mawu akuti “Ya” ndi chidule cha dzina lakuti Yehova.

Mʼchilankhulo choyambirira, “zowawa za pobereka.”

Kutanthauza, “Kuwawa.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Pakati pa madzulo awiri.”

Malita pafupifupi 2.2. Onani Zakumapeto B14.

Kapena kuti, “Mawa tidzasunga sabata.”

Kapena kuti, “anapuma pa.”

Zikuoneka kuti dzinali linachokera kumawu a Chiheberi amene amatanthauza kuti “Nʼchiyani ichi?”

Mʼchilankhulo choyambirira, “njere ya koriyanda.”

Kapena kuti, “Chikumbutso.” Zikuoneka kuti limeneli linali bokosi losungiramo zinthu zofunika zimene analemba.

Muyezo wa efa ndi wofanana ndi malita 22. Onani Zakumapeto B14.

Kutanthauza, “Kuyesa; Mayesero.”

Kutanthauza, “Kukangana.”

Kutanthauza, “Yehova Ndi Mtengo Wanga Wachizindikiro.”

Kutanthauza, “Ndi Mlendo Kumeneko.”

Kutanthauza, “Mulungu Wanga Ndi Mthandizi.”

Kapena kuti, “anawapsompsona.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “kuchokera mʼmanja mwa Iguputo.”

Zikuoneka kuti mawu amenewa akutanthauza tsiku limene ananyamuka ku Refidimu.

Mwina kulasidwa ndi muvi.

Mʼchilankhulo choyambirira, “asayandikire mkazi.”

Kapena kuti, “motsutsana ndi ine.” Mʼchilankhulo choyambirira, “motsutsana ndi nkhope yanga.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼmageti anu.”

Kupha uku ndi kupha munthu mwachiwembu osati mwalamulo.

Kapena kuti, “nsembe zanu zamtendere.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “kuti awomboledwe.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “kumupatsa mangawa a mu ukwati.”

Mabaibulo ena amati, “chida.”

Kapena kuti, “wavulala kwambiri.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Sekeli imodzi inali yofanana ndi magalamu 11.4. Onani Zakumapeto B14.

Kutanthauza kuti, kupita naye kwa oweruza oimira Mulungu woona.

Mwina chifukwa cha kusasamala kapena chifukwa cha zochitika zina zimene akanatha kuzipewa.

Kapena kuti, “mwana wopanda bambo.”

Kapena kuti, “wovutika.”

Kapena kuti, “Usanyoze.”

Kapena kuti, “wolamulira.”

Kapena kuti, “umboni umene anthu ambiri akupereka.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mawu abodza.”

Kapena kuti, “chifukwa sindidzagamula kuti munthu woipa alibe mlandu.”

Onani Zakumapeto B15.

Chimadziwikanso kuti Chikondwerero cha Masabata kapena Pentekosite.

Chimadziwikanso kuti Chikondwerero cha Misasa (Mahema).

Kapena kuti, “Ndipo ndidzachititsa kuti masiku a moyo wanu akhale okwanira.”

Kapena kuti, “ndidzachititsa kuti adani anu akulozetseni misana yawo.”

Mabaibulo ena amati, “kupanikizika; mantha aakulu.”

Umenewu ndi mtsinje wa Firate.

Kapena kuti, “mkuwa.”

Kapena kuti, “ubweya wa nkhosa wonyika mu utoto wapepo.”

Katumbu ndi nyama yaubweya yamʼmadzi, ndipo katumbu amene akutchulidwa pano ndi mtundu waukulu wa akatumbu amene amapezeka mʼnyanja zikuluzikulu.

Kapena kuti, “bokosi.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mikono iwiri ndi hafu.” Onani Zakumapeto B14.

Mʼchilankhulo choyambirira, “chikhatho chimodzi.” Onani Zakumapeto B14.

Talente imodzi inali yofanana ndi makilogalamu 34.2. Onani Zakumapeto B14.

Mʼchilankhulo choyambirira, “mikono 28.” Onani Zakumapeto B14.

Kapena kuti, “katani yotchinga.”

Kapena kuti, “Katani yotchinga.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mikono 5.” Onani Zakumapeto B14.

Kapena kuti, “mkuwa.”

Kapena kuti, “phulusa la mafuta,” kutanthauza phulusa losakanikirana ndi mafuta a nsembe.

Kapena kuti, “Mʼchihema chokumanako ndi Mulungu.” Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Mʼchilankhulo choyambirira, “amtima wa nzeru.”

Kapena kuti, “lamba wa mʼchiuno.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “chikhatho chimodzi.”

Imeneyi ndi miyala yamtengo wapatali mwina monga mwala wa huwakinto, opa ndi tomalini.

Kapena kuti, “lamba wa mʼchiuno.”

Kapena kuti, “lamba wa mʼchiuno.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

“Makangaza” ndi mtundu wa chipatso. Ena amati chimanga chachizungu.

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Mʼchilankhulo choyambirira, “ndipo udzaze manja awo.”

Kapena kuti, “zovala zamʼkati zofika.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”

Nʼkuthekanso kuti Mose anawauza kuti asambe.

Kapena kuti, “lamba wamʼchiuno.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “udzaze dzanja la Aroni ndi manja a ana ake.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “yakafungo kokhazika mtima pansi.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “kafungo kokhazika mtima pansi.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “udzaze manja awo.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mlendo,” kutanthauza munthu amene si wa mʼbanja la Aroni.

Mʼchilankhulo choyambirira, “udzaze manja awo.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “pakati pa madzulo awiri.”

Muyezo wa efa ndi wofanana ndi malita 22. Onani Zakumapeto B14.

Muyezo wa hini ndi wofanana ndi malita 3.67. Onani Zakumapeto B14

Mʼchilankhulo choyambirira, “pakati pa madzulo awiri.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “kafungo kokhazika mtima pansi.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mkono umodzi.” Onani Zakumapeto B14.

Kutanthauza kuti nyanga zimenezi sanazipangire padera nʼkuchita kuzilumikiza kuguwalo.

Sekeli imodzi inali yofanana ndi magalamu 11.4. Onani Zakumapeto B14.

Kapena kuti, “mogwirizana ndi sekeli yoyera.”

Gera imodzi inali yofanana ndi magalamu 0.57. Onani Zakumapeto B14.

Sekeli imodzi inali yofanana ndi magalamu 11.4. Onani Zakumapeto B14.

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Kapena kuti, “mogwirizana ndi sekeli yoyera.”

Muyezo wa hini ndi wofanana ndi malita 3.67. Onani Zakumapeto B14

Kapena kuti, “mafuta onunkhira ngati opangidwa ndi anthu ogwira ntchito yosakaniza mafuta.”

“Sitakate” ndi utomoni wonunkhira wa mitengo.

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Kapena kuti, “ngati mmene amachitira anthu ogwira ntchito yosakaniza mafuta.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “ndaitana potchula dzina.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “amtima wanzeru.”

Kapena kuti, “fano lagolide wosungunula.”

Kapena kuti, “fano lagolide wosungunula.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Dzazani manja anu.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “anavula.”

Kapena kuti, “Ndakusankha.”

Kapena kuti, “wachisomo.”

Kapena kuti, “wokhulupirika.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Kapena kuti, “Yehova, dzina lake ndi amafuna kuti anthu azidzipereka kwa iye yekha.”

Kapena kuti, “amene salekerera opikisana naye.”

Onani Zakumapeto B15.

Mʼchilankhulo choyambirira, “aliyense wotsegula mimba ya mayi ake.”

Kapena kuti, “muzisunga sabata.”

Kapena kuti, “Mawiki.”

Chimadziwikanso kuti Chikondwerero cha Misasa (Mahema).

Mʼchilankhulo choyambirira, “Mawu Khumi.”

Kapena kuti, “mkuwa.”

Katumbu ndi nyama yaubweya yamʼmadzi, ndipo katumbu amene akutchulidwa pano ndi mtundu waukulu wa akatumbu amene amapezeka mʼnyanja zikuluzikulu.

Mʼchilankhulo choyambirira, “amtima wanzeru.”

Kapena kuti, “anapereka nsembe yoyendetsa uku ndi uku.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mtima wanzeru.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mwamuna aliyense wamtima wanzeru.”

Zikuoneka kuti akunena Bezaleli.

Mʼchilankhulo choyambirira, “mikono 28.” Onani Zakumapeto B14.

Mʼchilankhulo choyambirira, “mikono iwiri ndi hafu.” Onani Zakumapeto B14.

Mʼchilankhulo choyambirira, “chikhatho chimodzi.” Onani Zakumapeto B14.

Talente imodzi inali yofanana ndi makilogalamu 34.2. Onani Zakumapeto B14.

Kutanthauza kuti nyanga zimenezi sanazipangire padera nʼkuchita kuzilumikiza kuguwalo.

Kapena kuti, “ngati opangidwa ndi anthu ogwira ntchito yosakaniza mafuta.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mikono 5.” Onani Zakumapeto B14.

Kutanthauza kuti nyanga zimenezi sanazipangire padera nʼkuchita kuzilumikiza kuguwalo.

Kapena kuti, “mkuwa.”

Amenewa anali magalasi odziyangʼanira amene ankawapanga ndi chitsulo chimene ankachisalalitsa kwambiri kuti nkhope ya munthu izioneka.

Talente imodzi inali yofanana ndi makilogalamu 34.2. Onani Zakumapeto B14.

Sekeli imodzi inali yofanana ndi magalamu 11.4. Onani Zakumapeto B14.

Kapena kuti, “mogwirizana ndi sekeli yoyera.”

Kapena kuti, “mogwirizana ndi sekeli yoyera.”

Kapena kuti, “mogwirizana ndi sekeli yoyera.”

Kapena kuti, “Kopa wa nsembe yoyendetsa uku ndi uku.”

Kapena kuti, “lamba wa mʼchiuno.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “chikhatho chimodzi.” Onani Zakumapeto B14.

Imeneyi ndi miyala yamtengo wapatali mwina monga mwala wa huwakinto, opa ndi tomalini.

Kapena kuti, “lamba wamʼchiuno.”

Kapena kuti, “lamba wamʼchiuno.”

“Makangaza” ndi mtundu wa chipatso. Ena amati chimanga chachizungu.

Kapena kuti, “zovala zamkati.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena