EZEKIELI
1 Mʼchaka cha 30, mʼmwezi wa 4, pa tsiku la 5 la mweziwo, pamene ndinali pakati pa anthu amene anali ku ukapolo+ pafupi ndi mtsinje wa Kebara,+ kumwamba kunatseguka ndipo ndinayamba kuona masomphenya a Mulungu. 2 Pa tsiku la 5 la mweziwo, mʼchaka cha 5 kuchokera pamene Mfumu Yehoyakini anatengedwa ukapolo,+ 3 Yehova analankhula ndi Ezekieli,* mwana wa wansembe Buzi, pamene anali mʼdziko la Akasidi+ pafupi ndi mtsinje wa Kebara. Kumeneko mphamvu za Yehova zinayamba kugwira ntchito pa iye.*+
4 Ndinaona mphepo yamkuntho+ ikuchokera kumpoto. Ndinaonanso mtambo waukulu komanso moto walawilawi*+ utazunguliridwa ndi kuwala. Pakati pa motowo panali chinachake chooneka ngati siliva wosakanikirana ndi golide.+ 5 Pakati pa motowo panali zinazake zooneka ngati angelo 4,*+ ndipo mngelo aliyense ankaoneka ngati munthu. 6 Mngelo aliyense anali ndi nkhope 4 komanso mapiko 4.+ 7 Mapazi a angelowo anali owongoka ndipo anali ooneka ngati mapazi a mwana wa ngʼombe. Mapaziwo ankawala ngati kopa wopukutidwa bwino.+ 8 Pansi pa mapiko 4 a angelowo panali manja a munthu ndipo manjawo anali mbali zonse 4. Angelowo anali ndi nkhope ndiponso mapiko. 9 Mapiko a angelowo ankagundana. Angelowo sankatembenuka akamayenda, mngelo aliyense ankangopita kutsogolo.+
10 Nkhope za angelowo zinkaoneka chonchi: Mngelo aliyense pa angelo 4 amenewo anali ndi nkhope ya munthu, nkhope ya mkango+ mbali yakumanja ndiponso nkhope ya ngʼombe+ yamphongo mbali yakumanzere. Mngelo aliyense pa angelo 4 amenewo analinso ndi nkhope+ ya chiwombankhanga.+ 11 Umu ndi mmene nkhope zawo zinalili. Mapiko awo anali otambasukira mʼmwamba. Mngelo aliyense anali ndi mapiko awiri ogundana, ndipo mapiko ena awiri ankaphimba matupi awo.+
12 Mngelo aliyense ankapita kutsogolo, ankapita kulikonse kumene mzimu ukufuna kuti apite.+ Angelowo sankatembenuka akamayenda. 13 Angelowo ankaoneka ngati makala oyaka moto. Pakati pa angelowo panali zinazake zooneka ngati miyuni ya moto wowala imene inkayenda kuchokera kwa mngelo wina kupita kwa mngelo wina ndipo mʼmotowo munkatuluka mphezi.+ 14 Angelowo akapita kwinakwake nʼkubwerako, mayendedwe awo ankaoneka ngati mphezi.
15 Pamene ndinkayangʼana angelowo, ndinangoona wilo limodzi lili pansi pambali pa mngelo wankhope 4 aliyense.+ 16 Mawilowo ankawala ngati mwala wa kulusolito, ndipo mawilo 4 onsewo ankaoneka mofanana. Anapangidwa mooneka ngati wilo lina lili pakati pa linzake.* 17 Mawilowo ankalowera kumbali iliyonse pambali zonse 4 ndipo sankafunika kuchita kukhota akamayenda. 18 Malimu a mawilowo anali aatali kwambiri moti anali ochititsa mantha. Malimu 4 onsewo anali ndi maso paliponse.+ 19 Angelo aja akamayenda, nawonso mawilowo ankayenda nawo limodzi. Angelowo akamakwera mʼmwamba kuchokera pansi, mawilowonso ankakwera mʼmwamba.+ 20 Angelowo ankapita kulikonse kumene mzimu ukufuna kuti apite, kulikonse kumene mzimuwo wapita. Mawilowo ankakwera mʼmwamba limodzi ndi angelowo chifukwa mzimu womwe unkatsogolera angelowo unkatsogoleranso mawilowo. 21 Angelowo akamayenda, mawilowonso ankayenda. Angelowo akaima, mawilowonso ankaima. Angelowo akakwera mʼmwamba kuchokera pansi, mawilowonso ankakwera mʼmwamba chifukwa mzimu womwe unkatsogolera angelowo unkatsogoleranso mawilowo.
22 Pamwamba pa mitu ya angelowo panali chinachake chooneka ngati thambo chimene chinayalidwa pamwamba pa mitu yawo. Chinthucho chinali chonyezimira ngati madzi oundana ochititsa chidwi.+ 23 Mapiko a angelo omwe anali pansi pa chinthu chooneka ngati thambocho, anali otambasukira mʼmwamba ndipo phiko lililonse linkagundana ndi linzake. Mngelo aliyense anali ndi mapiko awiri amene ankaphimba mbali imodzi ya thupi lake, ndipo mapiko ena awiri ankaphimba mbali ina yotsalayo. 24 Phokoso la mapiko awo linkamveka ngati phokoso la madzi omwe akuthamanga ndiponso ngati phokoso la Wamphamvuyonse.+ Angelowo akamayenda, ankamveka ngati phokoso la gulu la asilikali. Akaima, ankatsitsa mapiko awo pansi.
25 Pamwamba pa chinthu chooneka ngati thambo chimene chinali pamwamba pa mitu yawo pankamveka mawu. (Akaima, ankatsitsa mapiko awo pansi.) 26 Pamwamba pa chinthu chooneka ngati thambo chimene chinali pamwamba pa mitu yawo, panali chinachake chooneka ngati mwala wa safiro+ ndipo chinkaonekanso ngati mpando wachifumu.+ Pachinthu chooneka ngati mpando wachifumucho, panakhala winawake wooneka ngati munthu.+ 27 Ndinaona chinachake chowala ngati siliva wosakanikirana ndi golide,+ chimene chinkaoneka ngati moto umene ukuyaka kuchokera pa chimene chinkaoneka ngati chiuno chake kupita mʼmwamba. Komanso kuchokera mʼchiuno chake kupita mʼmunsi, ndinaona chinachake chooneka ngati moto.+ Pamalo onse omuzungulira panali powala 28 ngati utawaleza+ umene ukuoneka mumtambo pa tsiku la mvula. Umu ndi mmene kuwala kozungulira pamalopo kunkaonekera. Kunkaoneka ngati ulemerero wa Yehova.+ Nditaona zimenezo, ndinagwada nʼkuwerama mpaka nkhope yanga pansi. Kenako ndinayamba kumva mawu a winawake akulankhula.
2 Kenako iye anandiuza kuti: “Iwe mwana wa munthu,* imirira kuti ndikulankhule.”+ 2 Atalankhula nane, mzimu unalowa mwa ine ndipo unandipangitsa kuti ndiimirire+ kuti ndizitha kumva zomwe amene ankalankhula ndi ineyo ankanena.
3 Iye anapitiriza kundiuza kuti: “Iwe mwana wa munthu, ndikukutumiza kwa Aisiraeli,+ ku mitundu ya anthu amene andipandukira.+ Iwo ndi makolo awo akhala akuphwanya malamulo anga mpaka lero.+ 4 Ndikukutumiza kwa ana osamvera komanso ouma mtima+ ndipo ukawauze kuti, ‘Izi nʼzimene Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena.’ 5 Kaya akamvetsera kapena ayi, popeza iwo ndi anthu opanduka,+ adzadziwabe ndithu kuti pakati pawo panali mneneri.+
6 Koma iwe mwana wa munthu, usawaope+ ndipo usachite mantha ndi zimene akunena ngakhale kuti wazunguliridwa ndi anthu amene ali ngati minga*+ komanso ukukhala pakati pa zinkhanira. Usachite mantha ndi zimene akunena+ ndipo usaope nkhope zawo,+ chifukwa iwo ndi anthu opanduka. 7 Ukawauze mawu anga, kaya akamvetsera kapena ayi, chifukwa iwo ndi anthu opanduka.+
8 Koma iwe mwana wa munthu, mvetsera zimene ndikukuuza. Usapanduke ngati anthu opandukawa. Tsegula pakamwa pako kuti udye zimene ndikukupatsa.”+
9 Nditayangʼana, ndinaona dzanja litatambasukira kwa ine.+ Mʼdzanjalo munali mpukutu wolembedwa.+ 10 Atautambasula, ndinaona kuti mpukutuwo unali wolembedwa kumbali zonse.+ Mumpukutumo munalembedwa nyimbo zoimba polira, mawu odandaula ndi mawu olira.+
3 Kenako anandiuza kuti: “Iwe mwana wa munthu, idya chimene chili pamaso pakochi.* Idya mpukutu uwu ndipo upite kukalankhula ndi nyumba ya Isiraeli.”+
2 Choncho ndinatsegula pakamwa panga, ndipo iye anandipatsa mpukutuwo kuti ndidye. 3 Iye anapitiriza kundiuza kuti: “Iwe mwana wa munthu, idya mpukutu umene ndikukupatsawu kuti mimba yako ikhute.” Choncho ndinayamba kudya mpukutuwo ndipo unali wotsekemera ngati uchi.+
4 Iye anandiuza kuti: “Iwe mwana wa munthu, pita pakati pa nyumba ya Isiraeli ndipo ukawauze mawu anga. 5 Chifukwa sindikukutuma kwa anthu amene amalankhula chilankhulo chovuta kumva kapena chilankhulo chimene iwe sukuchidziwa, koma ndikukutuma ku nyumba ya Isiraeli. 6 Sindikukutuma kwa mitundu yambiri ya anthu amene amalankhula chilankhulo chovuta kumva kapena chilankhulo chimene sukuchidziwa, amene sungathe kumvetsetsa zimene akunena. Ndikanakhala kuti ndakutumiza kwa anthu amenewo, akanakumvera.+ 7 Koma a nyumba ya Isiraeli akakana kukumvera, chifukwa iwo sakufuna kundimvera.+ Anthu onse a nyumba ya Isiraeli ndi amakani komanso osamva.+ 8 Koma ndachititsa kuti nkhope yako ikhale yolimba mofanana ndi nkhope zawo, ndiponso chipumi chako kuti chikhale cholimba mofanana ndi zipumi zawo.+ 9 Ndachititsa kuti chipumi chako chikhale ngati mwala wa dayamondi, cholimba kuposa mwala wa nsangalabwi.+ Usawaope kapena kuchita mantha ndi nkhope zawo,+ chifukwa iwo ndi anthu opanduka.”
10 Iye anapitiriza kundiuza kuti: “Iwe mwana wa munthu, mvetsera mawu onse amene ndikukuuza ndipo uwaganizire mozama. 11 Pita pakati pa anthu a mtundu wako* amene anatengedwa kupita ku ukapolo+ ndipo ukalankhule nawo. Ukawauze kuti, ‘Izi nʼzimene Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa wanena,’ kaya akamvetsera kapena ayi.”+
12 Kenako mzimu unanditenga+ ndipo ndinayamba kumva mawu amphamvu kumbuyo kwanga ngati chimkokomo chachikulu akuti: “Ulemerero wa Yehova utamandike kumalo amene amakhala.” 13 Kenako ndinamva phokoso la mapiko a angelo pamene mapikowo ankakhulana.+ Ndinamvanso phokoso la mawilo amene anali pambali pawo+ komanso chimkokomo chachikulu. 14 Mzimu unandinyamula nʼkupita nane ndili wachisoni komanso wokwiya kwambiri. Dzanja la Yehova linandigwira mwamphamvu. 15 Choncho ndinapita kwa anthu amene anatengedwa kupita ku ukapolo omwe anali ku Tele-abibu. Anthuwa ankakhala pafupi ndi mtsinje wa Kebara.+ Ndinakhala nawo kumeneko masiku 7 nditasokonezeka maganizo.+
16 Masiku 7 atatha, Yehova anandiuza kuti:
17 “Iwe mwana wa munthu, ine ndakuika kuti ukhale mlonda wa nyumba ya Isiraeli.+ Choncho ukamva mawu ochokera pakamwa panga ukuyenera kuwachenjeza.+ 18 Ndikauza munthu woipa kuti, ‘Udzafa ndithu,’ koma iwe osalankhula naye nʼkumuchenjeza kuti asiye zoipa zimene akuchita kuti akhalebe ndi moyo,+ munthuyo adzafa chifukwa cha zolakwa zake popeza ndi woipa,+ koma iwe ndidzakuimba mlandu chifukwa cha magazi ake.*+ 19 Iweyo ukachenjeza munthu woipa koma iye osasiya zoipa zakezo ndi njira zake zoipa, munthuyo adzafa chifukwa cha zolakwa zake, koma iweyo udzapulumutsadi moyo wako.+ 20 Munthu amene amachita zinthu zabwino akasiya kuchita zabwinozo nʼkumachita zoipa,* ndidzamubweretsera tsoka ndipo adzafa.+ Ngati sunamuchenjeze, adzafa chifukwa cha tchimo lake ndipo zabwino zimene ankachita sizidzakumbukiridwa, koma magazi ake ndidzawafuna kuchokera kwa iwe.*+ 21 Koma ngati iweyo unachenjeza munthu wolungama kuti asachimwe, iye osachimwadi, munthuyo adzakhalabe ndi moyo chifukwa anachenjezedwa,+ ndipo iweyo udzakhala utapulumutsa moyo wako.”
22 Kenako dzanja la Yehova linafika pa ine kumeneko ndipo iye anandiuza kuti: “Nyamuka, pita kuchigwa ndipo ndikalankhula nawe kumeneko.” 23 Choncho ndinanyamuka nʼkupita kuchigwako ndipo ndinaona kuti ulemerero wa Yehova uli kumeneko.+ Ulemerero umenewu unali wofanana ndi umene ndinauona pafupi ndi mtsinje wa Kebara+ ndipo ndinagwada nʼkuwerama mpaka nkhope yanga pansi. 24 Kenako mzimu unalowa mwa ine nʼkuchititsa kuti ndiimirire,+ ndipo Mulungu anandiuza kuti:
“Pita ukadzitsekere mʼnyumba mwako. 25 Iwe mwana wa munthu, dziwa kuti anthu adzakumanga ndi zingwe kuti usapite pakati pawo. 26 Ndidzachititsa kuti lilime lako lidzaze mʼkamwa mwako ndipo sudzatha kulankhula kapena kuwadzudzula, chifukwa iwo ndi anthu opanduka. 27 Koma ndikamalankhula nawe ndizikutsegula pakamwa ndipo iweyo uziwauza kuti,+ ‘Izi nʼzimene Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa wanena.’ Wakumva amve,+ ndipo amene sakufuna kumva asamve, chifukwa iwo ndi anthu opanduka.”+
4 “Iwe mwana wa munthu, tenga njerwa ndipo uiike patsogolo pako. Panjerwapo ujambulepo mzinda wa Yerusalemu. 2 Umenye nkhondo ndi mzindawo+ ndipo umange mpanda womenyerapo nkhondo kuzungulira mzinda wonsewo.+ Umangenso malo okwera omenyerapo nkhondo+ komanso misasa ya asilikali. Uikenso zida zankhondo zogumulira mpanda wa mzindawo kuzungulira mzinda wonsewo.+ 3 Utenge chiwaya ndipo uchiike pakati pa iweyo ndi mzindawo kuti chikhale ngati khoma lachitsulo. Uziyangʼana mzindawo monyansidwa ndipo usonyeze zimene adani adzachite poukira mzindawo. Chimenechi chikhale chizindikiro ku mtundu wa Isiraeli.+
4 Kenako ugonere kumanzere kwako ndipo ugonere zolakwa za nyumba ya Isiraeli.+ Kwa masiku amene udzagonere kumanzereko, udzanyamula zolakwa zawo. 5 Ine ndidzafuna kuti uchite zimenezi kwa masiku 390, mogwirizana ndi zaka za kulakwa kwawo.+ Ndipo iweyo udzanyamula zolakwa za nyumba ya Isiraeli. 6 Udzakwanitse masiku onsewo.
Kenako udzagonere kumanja kwako, ndipo udzanyamule zolakwa za nyumba ya Yuda+ kwa masiku 40. Ndakupatsa tsiku limodzi kuti liimire chaka chimodzi. 7 Nkhope yako izidzayangʼana Yerusalemu+ atazunguliridwa ndi asilikali. Udzapinde malaya ako kuti dzanja lako lidzakhale pamtunda ndipo udzalosere zinthu zoipa zimene zidzachitikire mzindawo.
8 Ine ndidzakumanga ndi zingwe kuti usathe kutembenukira kumbali ina, mpaka utamaliza masiku ako ozungulira mzindawo.
9 Ndipo utenge tirigu, balere, nyemba zikuluzikulu, mphodza, mapira ndi sipeloti.* Zonsezo uziike mumphika umodzi kuti zikhale chakudya chako. Pa masiku 390 amene udzakhale ukugonera mbali imodzi uzidzadya chakudya chimenechi.+ 10 Tsiku lililonse uzidzadya chakudya chochita kuyeza. Uzidzadya chakudya chokwana masekeli 20.* Uzidzadya chakudyachi nthawi yofanana tsiku lililonse.
11 Uzidzamwa madzi ochita kuyeza, ndipo uzidzamwa makapu awiri okha.* Uzidzamwa madziwo nthawi yofanana tsiku lililonse.
12 Uzidzadya chakudyacho ngati mmene umadyera mkate wozungulira wa balere. Uzidzachiphika iwo akuona pogwiritsa ntchito tudzi touma ta anthu.” 13 Yehova anapitiriza kunena kuti: “Mofanana ndi zimenezi, Aisiraeli azidzadya chakudya chodetsedwa pakati pa anthu a mitundu ina kumene ndidzawabalalitsireko.”+
14 Kenako ndinanena kuti: “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, ndiloleni ndisachite zimenezo. Kuyambira ndili mwana mpaka pano sindinadzidetsepo podya nyama yopezeka itafa kapena nyama yochita kukhadzulidwa ndi chilombo,+ ndipo mʼkamwa mwanga simunalowepo nyama yodetsedwa.”+
15 Choncho iye anandiuza kuti: “Chabwino, ndikulola kuti uzigwiritsa ntchito ndowe za ngʼombe mʼmalo mwa tudzi ta anthu kuti uziphikira chakudya chako.” 16 Kenako anandiuza kuti: “Iwe mwana wa munthu, ine ndidzachititsa kuti chakudya chisowe* mu Yerusalemu.+ Anthu azidzadya chakudya chochita kuyeza ndipo adzachidya ali ndi nkhawa yaikulu.+ Azidzamwa madzi ochita kuyeza ali ndi mantha aakulu.+ 17 Zimenezi zikadzachitika azidzayangʼanizana modabwa posowa chakudya ndi madzi ndipo adzaonda chifukwa cha zolakwa zawo.”
5 “Iwe mwana wa munthu, tenga lupanga lakuthwa kuti uligwiritse ntchito ngati lezala lometera. Umete tsitsi lako ndi ndevu zako ndipo kenako utenge sikelo nʼkuyeza tsitsilo. Ukatero uligawe mʼmagawo atatu. 2 Gawo limodzi la magawo atatu a tsitsilo uliwotche pamoto mumzindawo, masiku ozungulira mzindawo akatha.+ Kenako utenge gawo lina la magawo atatuwo nʼkumalimenya ndi lupanga ukuzungulira mzindawo.+ Gawo lomaliza la magawo atatuwo uliuluze ndi mphepo ndipo ine ndilitsatira nditasolola lupanga.+
3 Pagawo lachitatuli utengepo tsitsi lochepa nʼkulikulunga mʼzovala zako. 4 Utengeponso tsitsi lina nʼkuliponya pamoto kuti lipse. Pamotowo, padzabuka moto umene udzafalikire kunyumba yonse ya Isiraeli.+
5 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: ‘Uyu ndi Yerusalemu. Ndamuika pakati pa anthu a mitundu ina ndipo wazunguliridwa ndi mayiko ena. 6 Iye anapandukira zigamulo zanga ndi malamulo anga pochita zoipa kuposa anthu amitundu inawo ndi mayiko amene amuzungulira.+ Anthu okhala mu Yerusalemu anakana zigamulo zanga ndipo sanatsatire malamulo anga.’
7 Choncho Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: ‘Chifukwa chakuti anthu inu munali ovuta kuposa anthu a mitundu ina amene anakuzungulirani, ndipo simunatsatire malamulo anga, kapena kutsatira zigamulo zanga, koma munatsatira zigamulo za anthu a mitundu ina amene anakuzungulirani,+ 8 izi nʼzimene Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena: “Ine ndakhala mdani wako mzinda iwe,+ ndipo ndidzakupatsa chilango anthu a mitundu ina akuona.+ 9 Chifukwa cha zinthu zonse zonyansa zimene umachita, mwa iwe ndidzachita zinthu zimene sindinachitepo ndiponso zimene sindidzachitanso.+
10 Choncho azibambo amene ali mumzindawo adzadya ana awo+ ndipo ana adzadya abambo awo. Ine ndidzakulanga ndipo anthu ako onse otsala ndidzawabalalitsira kumbali zonse.”’+
11 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: ‘Pali ine Mulungu wamoyo, chifukwa chakuti iwe unaipitsa malo anga opatulika ndi mafano ako onse onyansa komanso zinthu zonse zonyansa zimene unkachita,+ inenso ndidzakukana.* Diso langa silidzakumvera chisoni ndipo sindidzakuchitira chifundo.+ 12 Gawo limodzi la magawo atatu a anthu a mtundu wako lidzafa ndi mliri* kapena lidzafa ndi njala pakati pako. Gawo lina lidzaphedwa ndi lupanga mokuzungulira.+ Gawo lachitatu ndidzalibalalitsira kumbali zonse, ndipo ndidzalithamangitsa nditasolola lupanga.+ 13 Kenako mkwiyo wanga udzatha komanso ukali wanga pa iwo udzachepa ndipo ndidzakhutira.+ Ndikadzamaliza kuwasonyeza ukali wanga, iwo adzadziwa kuti ine Yehova ndalankhula chifukwa ndimafuna kuti anthu azidzipereka kwa ine ndekha basi.+
14 Iweyo ndidzakusandutsa bwinja ndipo uzidzanyozedwa ndi anthu a mitundu yokuzungulira komanso ndi munthu aliyense wodutsa.+ 15 Udzakhala chinthu chimene anthu azidzachinyoza komanso kuchichitira chipongwe.+ Zimene zidzakuchitikire zidzakhala chenjezo ndipo zidzabweretsa mantha kwa anthu a mitundu yokuzungulira. Zimenezi zidzachitika ndikadzapereka chiweruzo kwa iwe komanso kukulanga mokwiya ndiponso mwaukali. Ineyo Yehova ndi amene ndanena zimenezi.
16 Ndidzakutumizirani njala yomwe idzakupheni ngati mivi,+ ndipo ndidzachititsa kuti chakudya chisowe*+ moti njalayo idzafika poipa kwambiri. 17 Ndidzakutumizira njala ndi zilombo zolusa+ ndipo zidzakuphera ana ako. Mliri komanso kuphana zidzakhala paliponse ndipo ndidzakubweretsera lupanga.+ Ineyo Yehova ndi amene ndanena zimenezi.’”
6 Yehova anandiuzanso kuti: 2 “Iwe mwana wa munthu, yangʼana kumapiri a Isiraeli ndipo ulosere zinthu zimene zidzawachitikire. 3 Uwauze kuti, ‘Inu mapiri a Isiraeli, mvetserani zimene akunena Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa: Izi nʼzimene Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, akunena kwa mapiri, zitunda, mitsinje ndi zigwa: “Ine ndidzakubweretserani lupanga ndipo ndidzawononga malo anu okwezeka. 4 Maguwa anu ansembe adzagumulidwa, maguwa anu ofukizirapo zonunkhira adzaphwanyidwa+ ndipo mitembo ya anthu anu amene adzaphedwe ndidzaiponyera pamaso pa mafano anu onyansa.*+ 5 Mitembo ya Aisiraeli ndidzaiponyera pamaso pa mafano awo onyansa, ndipo mafupa anu ndidzawamwaza kuzungulira maguwa anu ansembe.+ 6 Mʼmalo onse amene mukukhala, mizinda idzawonongedwa.+ Malo okwezeka adzagumulidwa ndipo adzakhala mabwinja.+ Maguwa anu ansembe adzagumulidwa nʼkuphwanyidwa. Mafano anu onyansa adzawonongedwa, maguwa anu ofukizirapo zonunkhira adzagwetsedwa ndipo ntchito za manja anu zidzawonongedwa. 7 Anthu amene aphedwa adzagwa pakati panu,+ ndipo inu mudzadziwa kuti ine ndine Yehova.+
8 Koma ndidzachititsa kuti pakhale anthu ena opulumuka, chifukwa ena a inu simudzaphedwa ndi lupanga pakati pa anthu a mitundu ina mukadzabalalikira mʼmayiko osiyanasiyana.+ 9 Anthu amene adzapulumuke adzandikumbukira pakati pa anthu amitundu ina amene anawagwira ukapolo.+ Adzazindikira kuti zinandipweteka kwambiri mumtima chifukwa cha mtima wawo wosakhulupirika* womwe unachititsa kuti andipandukire+ komanso maso awo amene amalakalaka mafano awo onyansa.+ Iwo adzachita manyazi komanso kuipidwa chifukwa cha zinthu zonse zoipa ndi zonyansa zimene anachita.+ 10 Iwo adzadziwa kuti ine ndine Yehova komanso kuti zimene ndinanena kuti ndidzawabweretsera tsoka limeneli, sizinali nkhambakamwa chabe.”’+
11 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: ‘Ombani mʼmanja mowawidwa mtima ndipo pondani pansi posonyeza kuti muli ndi chisoni chachikulu. Mulire chifukwa cha zoipa zonse komanso zonyansa zimene Aisiraeli anachita chifukwa iwo adzaphedwa ndi lupanga, njala ndi mliri.+ 12 Yemwe ali kutali adzaphedwa ndi mliri. Yemwe ali pafupi adzaphedwa ndi lupanga. Yemwe wapulumuka zinthu zimenezi adzafa ndi njala, ndipo ndidzawasonyeza mkwiyo wanga wonse.+ 13 Iwo adzadziwa kuti ine ndine Yehova,+ mitembo ya anthu awo ikadzakhala pakati pa mafano awo onyansa, kuzungulira maguwa awo onse ansembe,+ paphiri lililonse lalitali, pansonga zonse za mapiri, pansi pa mtengo uliwonse waukulu wamasamba obiriwira, ndiponso pansi pa nthambi za mitengo ikuluikulu pamene ankaperekerapo nsembe zonunkhira kuti asangalatse mafano awo onse onyansa.+ 14 Ndidzatambasula dzanja langa nʼkuwalanga ndipo dziko lawo ndidzalisandutsa bwinja. Malo awo onse amene amakhala adzasanduka bwinja loipa kwambiri kuposa chipululu chimene chili pafupi ndi Dibula. Iwo adzadziwa kuti ine ndine Yehova.’”
7 Yehova anandiuzanso kuti: 2 “Iwe mwana wa munthu, Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wauza dziko la Isiraeli kuti: ‘Mapeto afika! Mapeto afikira mbali zonse za dzikoli. 3 Mapeto akufikira, ndipo ndisonyeza mkwiyo wanga wonse pa iwe. Ndidzakuweruza mogwirizana ndi njira zako ndiponso kukulanga chifukwa cha zinthu zonse zonyansa zimene umachita. 4 Diso langa silidzakumvera chisoni ndipo sindidzakuchitira chifundo.+ Ndidzakulanga mogwirizana ndi njira zako, moti udzakumana ndi mavuto chifukwa cha zinthu zonyansa zimene ukuchita.+ Udzadziwa kuti ine ndine Yehova.’+
5 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: ‘Tsoka likubwera! Kukubwera tsoka loti silinaonekepo.+ 6 Mapeto akubwera ndipo afika ndithu. Akufikira modzidzimutsa. Akubwera ndithu. 7 Inu anthu amene mukukhala mʼdzikoli, mapeto anu afika.* Nthawi ikubwera, tsiku lake layandikira.+ Mʼmapiri mukumveka phokoso lachisokonezo, osati lachisangalalo.
8 Ndikukhuthulira mkwiyo wanga posachedwapa,+ ndipo ndisonyeza mkwiyo wanga wonse pa iwe.+ Ndidzakuweruza mogwirizana ndi njira zako ndiponso kukulanga chifukwa cha zinthu zonse zonyansa zimene umachita. 9 Diso langa silidzakumvera chisoni ndipo sindidzakuchitira chifundo.+ Ndidzakulanga mogwirizana ndi njira zako moti udzakumana ndi mavuto chifukwa cha zinthu zonyansa zimene ukuchita. Udzadziwa kuti ine Yehova, ndi amene ndikukulanga.+
10 Taona, tsikulo likubwera.+ Mapeto anu afika.* Ndodo yachita maluwa ndipo kudzikuza kwaphuka. 11 Chiwawa chasanduka ndodo yolangira zinthu zoipa.+ Kaya ndi anthuwo, chuma chawo, kuchuluka kwawo kapena kutchuka kwawo, palibe chimene chidzapulumuke. 12 Nthawi idzakwana ndipo tsikulo lidzafika. Wogula asasangalale ndipo wogulitsa asalire, chifukwa mkwiyo wa Mulungu wayakira gulu lawo lonselo.*+ 13 Wogulitsa sadzabwerera pamalo amene anagulitsa ngakhale atadzapulumuka, chifukwa zinthu zonse zimene zili mʼmasomphenyawo zidzachitikira anthu onse. Palibe amene adzabwerere, ndipo chifukwa cha zolakwa zake,* palibe amene adzapulumutse moyo wake.
14 Iwo aliza lipenga+ ndipo aliyense wakonzeka, koma palibe amene akupita kunkhondo chifukwa mkwiyo wanga wayakira gulu lonselo.+ 15 Lupanga lidzapha anthu amene ali kunja kwa mzinda+ ndipo mliri ndi njala zidzapha amene ali mkati mwa mzinda. Aliyense amene ali kunja kwa mzinda adzaphedwa ndi lupanga ndipo amene ali mumzinda adzafa ndi njala komanso mliri.+ 16 Anthu awo amene adzapulumuke adzathawira kumapiri ndipo mofanana ndi njiwa zamʼzigwa, aliyense adzalira chifukwa cha zolakwa zake.+ 17 Manja awo onse adzafooka ndipo mawondo awo onse azidzangochucha madzi.*+ 18 Iwo avala ziguduli+ ndipo akungonjenjemera. Aliyense adzachititsidwa manyazi ndipo mitu yawo yonse idzakhala ndi mipala.*+
19 Siliva wawo adzamutaya mʼmisewu ndipo golide wawo adzanyansidwa naye. Siliva wawo kapena golide wawo sadzatha kuwapulumutsa pa tsiku limene Yehova adzasonyeze mkwiyo wake waukulu.+ Golide ndi siliva wawo sadzathetsa njala yawo kapena kuwakhutitsa, chifukwa chumacho chakhala ngati chinthu chopunthwitsa chimene chawachititsa kuti achimwe. 20 Iwo ankanyadira kukongola kwa zinthu zawo zodzikongoletsera. Ndipo pogwiritsa ntchito zinthu zimenezi* anapanga mafano awo onyansa.+ Nʼchifukwa chake ndidzachititse kuti zinthu zimenezi adzanyansidwe nazo. 21 Ndidzazipereka* mʼmanja mwa anthu ochokera mʼmayiko ena komanso kwa anthu oipa apadziko lapansi kuti azitenge, ndipo adzaziipitsa.
22 Ine ndidzayangʼana kumbali kuti ndisawaone+ ndipo adzaipitsa malo anga opatulika.* Akuba adzalowa mʼmalowo nʼkuwaipitsa.+
23 Panga unyolo+ chifukwa anthu osalakwa amene aweruzidwa mopanda chilungamo akuphedwa mʼdziko lonseli+ ndipo mumzinda mwadzaza chiwawa.+ 24 Ndidzabweretsa anthu oipa kwambiri a mitundu ina+ ndipo adzalanda nyumba zawo.+ Ndidzathetsa kunyada kwa anthu amphamvu ndipo malo awo opatulika adzaipitsidwa.+ 25 Anthu akadzayamba kuvutika, azidzafunafuna mtendere koma sadzaupeza.+ 26 Mʼdzikolo mudzakhala mavuto otsatizanatsatizana ndipo muzidzamveka mauthenga otsatizanatsatizana. Anthu azidzafuna kumva masomphenya kuchokera kwa mneneri.+ Koma wansembe sadzathanso kuphunzitsa malamulo* aphindu ndipo anthu achikulire sadzaperekanso malangizo othandiza.+ 27 Mfumu idzayamba kulira+ ndipo mtsogoleri adzagwidwa ndi mantha. Manja a anthu amʼdzikolo adzanjenjemera chifukwa cha mantha. Ndidzawachitira zinthu zogwirizana ndi njira zawo ndipo ndidzawaweruza mogwirizana ndi mmene ankaweruzira ena. Iwo adzadziwa kuti ine ndine Yehova.’”+
8 Mʼchaka cha 6, mʼmwezi wa 6, pa tsiku la 5 la mweziwo dzanja la Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, linandikhudza. Pa nthawiyo ndinali nditakhala mʼnyumba mwanga ndipo akuluakulu a Yuda anali atakhala pamaso panga. 2 Nditayangʼana ndinaona chinachake chooneka ngati moto. Ndipo moto unkayaka kuchokera pachimene chinkaoneka ngati chiuno chake kupita mʼmunsi.+ Kuchokera mʼchiuno mwake kupita mʼmwamba, maonekedwe ake anali owala ngati siliva wosakanikirana ndi golide.+ 3 Kenako iye anatambasula chinachake chooneka ngati dzanja ndipo anagwira tsitsi lakumutu kwanga nʼkundinyamula. Ndiyeno mzimu unandinyamulira mʼmalere pakati pa dziko lapansi ndi kumwamba, nʼkundipititsa ku Yerusalemu mʼmasomphenya ochokera kwa Mulungu. Mzimuwo unandifikitsa pakhomo la geti la bwalo lamkati+ loyangʼana kumpoto pamene panali fano loimira nsanje, limene limachititsa nsanje.+ 4 Kumeneko ndinaonako ulemerero wa Mulungu wa Isiraeli,+ wofanana ndi umene ndinaona kuchigwa uja.+
5 Kenako iye anandiuza kuti: “Iwe mwana wa munthu, kweza maso ako uyangʼane kumpoto.” Choncho ndinakweza maso anga nʼkuyangʼana kumpoto, ndipo ndinaona kuti kumpoto kwa geti la guwa lansembe kunali fano loimira nsanje lija pakhomo la getilo. 6 Iye anandiuza kuti: “Iwe mwana wa munthu, kodi ukuona zinthu zoipa komanso zonyansa kwambiri zimene anthu a nyumba ya Isiraeli akuchita kuno,+ zimene zikupangitsa kuti nditalikirane ndi malo anga opatulika?+ Koma uonanso zinthu zina zoipa zomwe ndi zonyansa kwambiri kuposa zimenezi.”
7 Kenako anandipititsa pakhomo lolowera mʼbwalo ndipo nditayangʼana ndinaona bowo pakhoma. 8 Iye anandiuza kuti: “Iwe mwana wa munthu, tabowola khomalo.” Ine ndinabowoladi khomalo ndipo ndinaona khomo. 9 Iye anandiuza kuti: “Lowa uone zinthu zoipa ndi zonyansa zimene anthu akuchita kuno.” 10 Choncho ndinalowa ndipo nditayangʼana ndinaona zithunzi za zinthu zosiyanasiyana zokwawa, nyama zonyansa+ komanso mafano onse onyansa* a Aisiraeli.+ Zithunzizo zinajambulidwa pamakoma onse mochita kugoba. 11 Ndipo akuluakulu 70 a nyumba ya Isiraeli anali ataimirira patsogolo pa mafanowo. Pakati pawo panalinso Yaazaniya mwana wa Safani.+ Aliyense ananyamula chiwaya chofukizira nsembe mʼmanja mwake ndipo utsi wonunkhira wa zofukizazo unkakwera mʼmwamba.+ 12 Iye anandiuza kuti: “Iwe mwana wa munthu, kodi waona zimene akuluakulu a Isiraeli akuchita mumdima? Kodi waona zimene aliyense wa iwo akuchita mʼzipinda zake zamkati mmene muli mafano ake? Iwo akunena kuti, ‘Yehova sakutiona. Yehova wachokamo mʼdziko muno.’”+
13 Iye anapitiriza kundiuza kuti: “Uonanso zinthu zina zoipa komanso zonyansa kwambiri zimene akuchita.” 14 Choncho anandipititsa pakhomo la geti la nyumba ya Yehova limene linali mbali yakumpoto ndipo kumeneko ndinaona azimayi atakhala pansi nʼkumalirira mulungu wotchedwa Tamuzi.
15 Iye anandiuzanso kuti: “Iwe mwana wa munthu, kodi ukuona zimenezi? Uonanso zinthu zina zoipa zomwe ndi zonyansa kwambiri kuposa zimenezi.”+ 16 Choncho anandipititsa kubwalo lamkati la nyumba ya Yehova.+ Ndiyeno ndinaona kuti pakhomo lolowera mʼkachisi wa Yehova, pakati pa khonde ndi guwa lansembe, panali amuna pafupifupi 25 atafulatira kachisi wa Yehova ndipo nkhope zawo zinali zitayangʼana kumʼmawa. Iwo ankagwadira dzuwa limene linali kumʼmawa.+
17 Iye anandiuza kuti: “Iwe mwana wa munthu, kodi waona zimenezi? Kodi ndi chinthu chachingʼono kuti anthu a nyumba ya Yuda azichita zinthu zonyansazi? Kodi ndi chinthu chachingʼono kuti adzaze dzikoli ndi chiwawa+ nʼkupitiriza kundikwiyitsa? Anthuwatu akulozetsa nthambi* pamphuno panga. 18 Choncho ineyo ndidzawalanga nditakwiya kwambiri. Diso langa silidzawamvera chisoni ndipo sindidzawachitira chifundo.+ Ngakhale iwo adzandilirire mofuula, ine sindidzamva.”+
9 Kenako iye analankhula mokuwa ine ndikumva, kuti: “Itana anthu amene akuyenera kupereka chilango pamzindawu. Aliyense abwere atanyamula chida chake chowonongera!”
2 Ndiyeno ndinaona amuna 6 akubwera kuchokera kugeti lakumtunda+ loyangʼana kumpoto, aliyense atanyamula chida chake chowonongera. Pakati pawo panali munthu mmodzi atavala zovala zansalu ndipo mʼchiuno mwake munali kachikwama ka mlembi, konyamuliramo inki ndi zolembera. Anthuwo analowa mkati nʼkuima pambali pa guwa lansembe lakopa.*+
3 Kenako ulemerero wa Mulungu wa Isiraeli+ unachoka pamwamba pa akerubi pamene unali ndipo unapita pakhomo la malo opatulika.+ Ndiyeno Mulungu anayamba kulankhula mofuula kwa munthu amene anavala zovala zansalu uja, yemwe mʼchiuno mwake munali kachikwama ka mlembi konyamuliramo inki ndi zolembera. 4 Yehova anauza munthu uja kuti: “Uyendeyende mumzinda wonse wa Yerusalemu ndipo ulembe chizindikiro pazipumi za anthu amene akuusa moyo komanso kubuula+ chifukwa cha zonyansa zonse zimene zikuchitika mumzindawu.”+
5 Ndiyeno iye anauza amuna ena aja ine ndikumva, kuti: “Mʼtsatireni ameneyu. Muyendeyende mumzindamo nʼkumapha anthu. Diso lanu lisamve chisoni ndipo musasonyeze aliyense chifundo.+ 6 Muphe amuna achikulire, anyamata, anamwali, tiana ndi azimayi ndipo pasatsale aliyense.+ Koma musayandikire munthu aliyense amene ali ndi chizindikiro+ ndipo muyambire pamalo anga opatulika.”+ Choncho iwo anayambira kupha akuluakulu amene anali kutsogolo kwa nyumbayo.+ 7 Kenako anawauza kuti: “Ipitsani nyumbayi ndipo mudzaze mabwalo ake ndi mitembo ya anthu ophedwa.+ Pitani!” Choncho iwo anapitadi nʼkukapha anthu mumzindamo.
8 Pamene amunawo ankapha anthu, ine ndekha ndi amene ndinatsala ndi moyo. Choncho ndinagwada nʼkuwerama mpaka nkhope yanga pansi ndipo ndinafuula kuti: “Mayo ine, Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa! Kodi muwononga anthu onse amene anatsala mu Isiraeli pamene mukukhuthulira ukali wanu pa Yerusalemu?”+
9 Iye anandiyankha kuti: “Zolakwa za nyumba ya Isiraeli ndi Yuda nʼzazikulu kwambiri.+ Dziko lawo ladzaza ndi kukhetsa magazi+ ndipo mumzindamo mwadzaza zinthu zopanda chilungamo.+ Iwo akunena kuti, ‘Yehova wachokamo mʼdziko muno ndipo Yehova sakuona.’+ 10 Koma ine diso langa silimva chisoni ndipo sindiwasonyeza chifundo.+ Ndiwabwezera mogwirizana ndi zochita zawo.”
11 Kenako ndinaona munthu amene anavala zovala zansalu uja, yemwe mʼchiuno mwake munali kachikwama konyamuliramo inki ndi zolembera atabwera, ndipo ananena kuti: “Ndachita zonse zimene munandilamula.”
10 Pamene ndinkaona masomphenyawo, ndinaona kuti pamwamba pa thambo limene linali pamwamba pa mitu ya akerubi, panali chinachake chooneka ngati mwala wa safiro. Chinthucho chinkaoneka ngati mpando wachifumu.+ 2 Kenako Mulungu anauza munthu amene anavala zovala zansalu uja+ kuti: “Pita pakati pa mawilo,+ pansi pa akerubi. Ukatengepo makala amoto+ odzaza manja ako onse awiri kuchokera pakati pa akerubiwo, ndipo ukawaponye pamzindawo.”+ Choncho iye anapitadi ine ndikuona.
3 Pamene munthuyo anapita pakati pawo, akerubiwo anali ataima mbali yakumanja kwa nyumba yopatulika ndipo mtambo unadzaza bwalo lonse lamkati. 4 Ndiyeno ulemerero wa Yehova+ unachoka pa akerubi nʼkupita pakhomo la nyumba yopatulika ndipo mtambo unayamba kudzaza nyumbayo pangʼonopangʼono.+ Komanso ulemerero wowala wa Yehova unadzaza mʼbwalo lonse la nyumbayo. 5 Phokoso la mapiko a akerubiwo linkamveka mʼbwalo lakunja ndipo linkamveka ngati mmene mawu a Mulungu Wamphamvuyonse amamvekera akamalankhula.+
6 Kenako Mulungu analamula munthu amene anavala zovala zansalu uja kuti: “Tenga moto pakati pa mawilo, pakati pa akerubi.” Ndipo munthuyo anapita nʼkukaima pambali pa wilo. 7 Ndiyeno mmodzi wa akerubiwo anatambasulira dzanja lake pamoto umene unali pakati pa akerubiwo.+ Iye anatenga motowo pangʼono nʼkuuika mʼmanja mwa munthu amene anavala zovala zansalu uja+ ndipo munthuyo anautenga nʼkuchoka. 8 Pansi pa mapiko a akerubiwo panali chinachake chooneka ngati manja a munthu.+
9 Pamene ndinkaona masomphenyawo, ndinaona kuti pambali pa akerubiwo panali mawilo 4. Pambali pa kerubi aliyense panali wilo limodzi ndipo mawilowo ankaoneka kuti akuwala ngati mwala wa kulusolito.+ 10 Mawilo 4 onsewo ankaoneka mofanana. Ankaoneka ngati wilo lina lili pakati pa wilo linzake. 11 Mawilowo akamayenda ankatha kulowera kumbali iliyonse pa mbali zonse 4 popanda kutembenuka chifukwa ankatha kupita kumene mitu ya akerubiwo yayangʼana popanda kutembenuka. 12 Mʼmatupi onse a akerubiwo, kumsana kwawo, mʼmanja mwawo, mʼmapiko awo ndiponso mʼmawilo a akerubi onse 4 munali maso paliponse.+ 13 Kenako ndinamva mawu akuitana mawilowo kuti, “Mawilo inu!”
14 Kerubi aliyense anali ndi nkhope 4. Nkhope yoyamba inali ya kerubi. Nkhope yachiwiri inali ya munthu. Nkhope yachitatu inali ya mkango ndipo nkhope ya 4 inali ya chiwombankhanga.+
15 Akerubiwo anali angelo omwe aja amene ndinawaona kumtsinje wa Kebara.+ Akerubiwo akanyamuka kukwera mʼmwamba 16 kapena akamayenda, mawilo aja ankayenda nawo limodzi ali pambali pawo. Akerubiwo akakweza mapiko awo kuti akwere mʼmwamba, mawilowo sankatembenuka kapena kuchoka pambali pawo.+ 17 Akerubiwo akaima, mawilonso ankaima. Akerubiwo akakwera mʼmwamba, mawilonso ankakwera nawo limodzi, chifukwa mzimu womwe unkatsogolera angelowo unkatsogoleranso mawilowo.
18 Kenako ulemerero wa Yehova+ unachoka pakhomo la nyumba yopatulika nʼkukaima pamwamba pa akerubiwo.+ 19 Tsopano akerubi aja anakweza mʼmwamba mapiko awo nʼkunyamuka kuchoka pansi ine ndikuona. Pamene amanyamuka, mawilo aja anali pambali pawo. Kenako iwo anakaima pakhomo lakumʼmawa la geti la nyumba ya Yehova ndipo ulemerero wa Mulungu wa Isiraeli unali pamwamba pawo.+
20 Amenewa anali angelo amene ndinawaona pansi pa mpando wachifumu wa Mulungu wa Isiraeli kumtsinje wa Kebara,+ choncho ndinadziwa kuti anali akerubi. 21 Angelo onse 4 anali ndi nkhope 4 komanso mapiko 4. Ndipo pansi pa mapiko awo panali chinachake chooneka ngati manja a munthu.+ 22 Maonekedwe a nkhope zawo anali ofanana ndi a nkhope zimene ndinaziona mʼmphepete mwa mtsinje wa Kebara.+ Mngelo aliyense ankapita kutsogolo basi.+
11 Kenako mzimu unandinyamula nʼkupita nane kugeti la nyumba ya Yehova limene linayangʼana kumʼmawa.+ Pakhomo la getilo ndinaonapo amuna 25 omwe anali akalonga+ ndipo pakati pawo panali Yaazaniya mwana wa Azuri ndi Pelatiya mwana wa Benaya. 2 Ndiyeno Mulungu anandiuza kuti: “Iwe mwana wa munthu, amuna amenewa ndi amene akukonza chiwembu ndiponso amene akupereka malangizo oipa mumzindawu. 3 Iwo akunena kuti: ‘Ino ndi nthawi yomanga nyumba.+ Mzindawu* uli ngati mphika*+ ndipo ifeyo tili ngati nyama mumphikamo.’
4 Choncho iweyo ulosere zinthu zoipa zimene zidzawachitikire. Losera, iwe mwana wa munthu.”+
5 Kenako mzimu wa Yehova unafika pa ine+ ndipo iye anandiuza kuti: “Unene kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Inu anthu a nyumba ya Isiraeli, zimene mwanena ndi zoona ndipo ine ndikudziwa zimene mukuganiza. 6 Inuyo mwachititsa kuti anthu ambiri afe mumzindawu ndipo mwadzaza misewu yake ndi anthu akufa.”’”+ 7 “Choncho Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Anthu akufa amene mwawamwaza mumzindawu ndi amene ali nyama ndipo mzindawu ndi mphika.+ Koma inuyo mudzatulutsidwa mumzindawu.’”
8 “‘Inu mukuopa lupanga+ koma ine ndidzachititsa kuti muphedwe ndi lupanga,’ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. 9 ‘Ine ndidzakutulutsani mumzindawu nʼkukuperekani mʼmanja mwa anthu ochokera kudziko lina ndipo ndidzakulangani.+ 10 Mudzaphedwa ndi lupanga.+ Ndidzakuweruzirani mʼmalire a Isiraeli+ ndipo mudzadziwa kuti ine ndine Yehova.+ 11 Kwa inu, mzindawu sudzakhala mphika ndipo inuyo simudzakhala nyama mkati mwa mphikawo. Ndidzakuweruzirani mʼmalire a Isiraeli. 12 Inuyo mudzadziwa kuti ine ndine Yehova, chifukwa simunasunge malamulo anga ndiponso simunatsatire zigamulo zanga.+ Koma inu munatsatira zigamulo za mitundu ya anthu amene akuzungulirani.’”+
13 Nditangomaliza kulosera, Pelatiya mwana wa Benaya anamwalira. Choncho ine ndinagwada nʼkuwerama mpaka nkhope yanga pansi, nʼkufuula kuti: “Mayo ine, inu Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa! Kodi mukufuna kuwononga Aisiraeli amene atsalawa?”+
14 Yehova analankhulanso nane kuti: 15 “Iwe mwana wa munthu, abale ako enieni, azichimwene ako amene ali ndi ufulu wowombola, limodzi ndi nyumba yonse ya Isiraeli, auzidwa ndi anthu amene akukhala ku Yerusalemu kuti, ‘Pitani kutali ndi Yehova. Dzikoli ndi lathu. Laperekedwa kwa ife kuti likhale lathu.’ 16 Choncho uwauze kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Ngakhale kuti ndawachotsa nʼkuwapititsa kutali kuti azikakhala pakati pa mitundu yosiyanasiyana ya anthu ndipo ndawabalalitsira mʼmayiko osiyanasiyana,+ ine ndidzakhala malo opatulika kwa iwo kwa kanthawi kochepa, kumayiko amene iwo apitako.”’”+
17 Choncho uwauze kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Kuwonjezera pamenepo ndidzakusonkhanitsani kuchokera kwa anthu a mitundu yosiyanasiyana ndiponso kuchokera mʼmayiko amene ndinakubalalitsiraniko ndipo ndidzakupatsani dziko la Isiraeli.+ 18 Iwo adzabwerera mʼdzikomo ndipo adzachotsamo mafano onse onyansa komanso adzasiya zinthu zonse zonyansa zimene amachita.+ 19 Ndidzawapatsa mtima umodzi+ ndipo ndidzaika mzimu watsopano mwa iwo.+ Ndidzachotsa mtima wamwala mʼmatupi awo+ nʼkuwapatsa mtima wamnofu,*+ 20 kuti azidzatsatira malamulo anga, azidzasunga komanso kumvera zigamulo zanga. Akadzatero adzakhala anthu anga ndipo ine ndidzakhala Mulungu wawo.”’
21 “‘“Koma amene atsimikiza mumtima mwawo kuti apitirize kutsatira mafano awo onyansa komanso kuchita zinthu zonyansa, ndidzawabwezera mogwirizana ndi zochita zawo,” akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.’”
22 Ndiyeno akerubi aja anakweza mapiko awo mʼmwamba ndipo mawilo anali pambali pawo.+ Ulemerero wa Mulungu wa Isiraeli unali pamwamba pawo.+ 23 Kenako ulemerero wa Yehova+ unakwera mʼmwamba kuchoka mumzindawo nʼkukaima pamwamba pa phiri, kumʼmawa kwa mzindawo.+ 24 Ndiyeno mzimu unandinyamula nʼkukandisiya kudziko la Kasidi kumene kunali anthu ogwidwa ukapolo. Zimenezi zinachitika mʼmasomphenya amene ndinaona kudzera mwa mzimu wa Mulungu. Kenako masomphenya amene ndinaonawo anazimiririka. 25 Pambuyo pake, ndinayamba kuuza anthu amene anagwidwa ukapolowo zinthu zonse zimene Yehova anandionetsa.
12 Yehova analankhulanso nane kuti: 2 “Iwe mwana wa munthu, ukukhala pakati pa anthu opanduka. Maso ali nawo koma saona, makutu ali nawo koma samva+ chifukwa ndi anthu opanduka.+ 3 Koma iweyo mwana wa munthu, longedza katundu wako woti upite naye ku ukapolo. Ndiyeno upite ku ukapolo masana anthuwo akuona. Uchoke kwanu kupita ku ukapolo kumalo ena, iwo akuona. Mwina azindikira tanthauzo lake ngakhale kuti iwo ndi anthu opanduka. 4 Masana iwo akuona, utulutse katundu wako amene walongedza kuti upite naye ku ukapolo. Ndiyeno madzulo iwo akuona, unyamuke ngati munthu amene watengedwa kupita ku ukapolo.+
5 Ubowole khoma iwo akuona nʼkutulutsirapo katundu wako.+ 6 Unyamule katunduyo paphewa iwo akuona ndipo umutulutse kuli mdima. Uphimbe nkhope yako kuti usaone pansi chifukwa ndakuika kuti ukhale chizindikiro ku mtundu wa Isiraeli.”+
7 Ine ndinachita zonse zomwe anandilamula. Masana ndinatulutsa katundu wanga ngati katundu wopita naye ku ukapolo ndipo madzulo ndinabowola khoma ndi manja. Kutagwa mdima, ndinatulutsa katundu wanga ndipo ndinamunyamula paphewa iwo akuona.
8 Mʼmawa Yehova analankhulanso nane kuti: 9 “Iwe mwana wa munthu, kodi anthu opanduka a nyumba ya Isiraeli sanakufunse kuti, ‘Kodi ukuchita chiyani?’ 10 Uwauze kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Uthenga uwu ndi wokhudza mtsogoleri+ amene ali mu Yerusalemu ndi anthu onse a nyumba ya Isiraeli amene ali mumzindawu.”’
11 Uwauze kuti, iweyo ndi chizindikiro chawo.+ Zimene iwe wachitazi ndi zimenenso zidzawachitikire iwowo. Iwo adzapita ku ukapolo, kudziko lina.+ 12 Mtsogoleri amene ali pakati pawo adzanyamula katundu wake paphewa nʼkuchoka kuli mdima. Adzabowola khoma nʼkutulutsirapo katundu wake.+ Iye adzaphimba nkhope kuti asaone pansi. 13 Ine ndidzamuponyera ukonde wanga ndipo iye adzakodwa mu ukonde wanga wosakira.+ Kenako ndidzamupititsa ku Babulo, kudziko la Akasidi. Koma iye sadzaliona dzikolo ndipo adzafera komweko.+ 14 Anthu onse amene amuzungulira, amene amamuthandiza ndiponso asilikali ake, ndidzawabalalitsira kumbali zonse+ ndipo ndidzasolola lupanga kuti ndiwathamangitse.+ 15 Iwo adzadziwa kuti ine ndine Yehova ndikadzawabalalitsira ku mitundu ina ya anthu ndi kumayiko ena. 16 Koma ndidzapulumutsa anthu ochepa pakati pawo kuti asaphedwe ndi lupanga, njala komanso mliri. Ndidzachita zimenezi kuti akafotokoze pakati pa anthu amitundu ina kumene adzapite zokhudza zinthu zonse zonyansa zimene ankachita ndipo adzadziwa kuti ine ndine Yehova.”
17 Ndiyeno Yehova analankhulanso nane kuti: 18 “Iwe mwana wa munthu, idya chakudya chako ukunjenjemera ndipo umwe madzi uli ndi mantha ndiponso nkhawa.+ 19 Anthu amʼdzikoli uwauze kuti, ‘Izi nʼzimene Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kwa anthu amene akukhala mu Yerusalemu, mʼdziko la Isiraeli: “Iwo adzadya chakudya chawo ali ndi nkhawa ndipo adzamwa madzi ali ndi mantha aakulu. Izi zidzachitika chifukwa dziko lawo lidzakhala bwinja lokhalokha+ chifukwa cha zinthu zachiwawa zimene anthu onse amene akukhala mmenemo akuchita.+ 20 Mizinda imene mukukhala anthu idzawonongedwa ndipo dzikolo lidzangokhala bwinja lokhalokha.+ Inu mudzadziwa kuti ine ndine Yehova.”’”+
21 Yehova analankhulanso nane kuti: 22 “Iwe mwana wa munthu, kodi mwambi umene anthu amʼdziko la Isiraeli mukunena wakuti, ‘Masiku akupita koma palibe masomphenya amene akwaniritsidwa,’+ umatanthauza chiyani? 23 Choncho uwauze kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Ine ndidzathetsa mwambi umenewu ndipo sadzaunenanso ngati mwambi mu Isiraeli.”’ Komano uwauze kuti, ‘Masiku ayandikira+ ndipo masomphenya onse adzakwaniritsidwa.’ 24 Chifukwa mʼnyumba ya Isiraeli simudzakhalanso masomphenya abodza kapena kulosera kwachiphamaso.*+ 25 ‘“Chifukwa ine Yehova ndidzalankhula ndipo mawu aliwonse amene ndidzalankhule adzachitikadi popanda kuzengereza.+ Mʼmasiku anu,+ inu a mʼnyumba yopanduka, ine ndidzanena mawu nʼkuwakwaniritsa,” akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.’”
26 Yehova analankhulanso nane kuti: 27 “Iwe mwana wa munthu, anthu a ku Isiraeli akunena kuti, ‘Masomphenya amene ukuona adzachitika kutsogolo ndipo ukulosera zinthu zimene zidzachitike mʼtsogolo kwambiri.’+ 28 Choncho uwauze kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “‘Palibe mawu aliwonse omwe ndalankhula amene sadzachitika pa nthawi yake. Zonse zimene ndanena zidzachitika,’ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”’”
13 Yehova anandiuzanso kuti: 2 “Iwe mwana wa munthu, losera zokhudza aneneri a mu Isiraeli+ ndipo anthu amene akulosera zamʼmutu mwawo+ uwauze kuti, ‘Imvani mawu a Yehova. 3 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Tsoka kwa aneneri opusa, amene akungolosera zamʼmutu mwawo pamene sanaone chilichonse.+ 4 Iwe Isiraeli, aneneri ako akhala ngati nkhandwe zamʼmabwinja. 5 Simudzapita mʼmalo ogumuka a mipanda yamiyala kuti mukamangirenso nyumba ya Isiraeli+ malo amene anagumukawo, nʼcholinga choti Aisiraeli adzapulumuke pa nkhondo pa tsiku la Yehova.”+ 6 “Iwo aona masomphenya abodza ndipo alosera zonama. Akunena kuti, ‘Yehova wanena kuti,’ pamene Yehova sanawatume, ndipo akuyembekeza kuti zimene anenazo zichitika.+ 7 Kodi masomphenya amene mwaonawa si abodza ndipo zimene mwaloserazi si zonama pamene mukunena kuti, ‘Yehova wanena kuti,’ pamene ine sindinanene chilichonse?”’
8 Choncho Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “‘Chifukwa choti mwalankhula zabodza ndipo masomphenya anu ndi onama, ine ndithana nanu,’ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”+ 9 Dzanja langa likulimbana ndi aneneri amene masomphenya awo ndi abodza ndiponso amene akulosera zonama.+ Iwo sadzakhala mʼgulu la anthu amene ndimawakonda ndipo sadzalembedwa mʼbuku la mayina a anthu a nyumba ya Isiraeli. Komanso sadzabwerera kudziko la Isiraeli ndipo mudzadziwa kuti ine ndine Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.+ 10 Zonsezi zidzachitika chifukwa chakuti iwo asocheretsa anthu anga ponena kuti, “Tili pa mtendere!” koma palibe mtendere.+ Munthu akamanga khoma lachipinda losalimba, iwo akumalipaka laimu.’*+
11 Uza anthu amene akupaka laimuwo kuti khomalo lidzagwa. Kudzagwa mvula yamphamvu, kudzagwanso matalala akuluakulu* ndipo mphepo yamkuntho idzagwetsa khomalo.+ 12 Ndiyeno khomalo likadzagwa, anthu adzakufunsani kuti, ‘Kodi laimu amene munapaka uja ali kuti?’+
13 Choncho Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: ‘Ndidzatumiza mphepo yamkuntho yamphamvu komanso mvula yambiri posonyeza mkwiyo wanga. Ndidzatumiza matalala akuluakulu kuti awononge khomalo chifukwa ndakwiya kwambiri. 14 Khoma limene mwalipaka laimulo, ndidzaligwetsa pansi ndipo maziko ake adzaonekera. Mzindawo ukamadzawonongedwa, inuyo mudzafera momwemo. Ndipo mudzadziwa kuti ine ndine Yehova.
15 Ndikadzasonyeza mkwiyo wanga wonse pakhomalo ndiponso pa anthu amene analipaka laimuwo, ndidzakuuzani kuti: “Khoma lija kulibe komanso anthu amene analipaka laimu aja kulibenso.+ 16 Aneneri a mu Isiraeli adzakhala atawonongedwa. Aneneri amenewa ndi omwe akulosera zokhudza Yerusalemu nʼkumaona masomphenya oti mumzindawo muli mtendere, pamene mulibe mtendere,”’+ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.
17 Koma iwe mwana wa munthu, yangʼana ana aakazi a anthu a mtundu wako, amene akulosera zamʼmutu mwawo ndipo ulosere zoipa zimene zidzawachitikire. 18 Uwauze kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Tsoka akazi amene akusoka zinthu zovala mʼmikono* yonse ndi kupanga nsalu zophimba kumutu za mitu ya masaizi osiyanasiyana nʼcholinga choti akole anthuwo mumsampha nʼkuwapha. Kodi mukusaka miyoyo ya anthu anga nʼkumayesetsa kuti mupulumutse miyoyo yanu? 19 Inu mukundinyozetsa pamaso pa anthu anga chifukwa cha balere wongodzaza mʼmanja ndi nyenyeswa za mkate.+ Inu mukupha anthu amene sakuyenera kufa, ndipo mukusiya anthu amene sakuyenera kukhala ndi moyo. Mukuchita zimenezi ponamiza anthu anga amene akumvetsera mabodza anuwo.”’+
20 Choncho Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: ‘Akazi inu, ine ndikudana ndi zinthu zanu zovala mʼmikono, zimene mukuzigwiritsa ntchito potchera anthu msampha ngati kuti ndi mbalame. Ndizichotsa mʼmikono mwanu nʼkumasula anthu amene mwawatchera msampha ngati mbalame. 21 Ndingʼamba nsalu zanu zophimba kumutu ndi kulanditsa anthu anga mʼmanja mwanu. Iwo sadzakhalanso ngati zinthu zoti muzidzazisaka nʼkuzigwira ndipo mudzadziwa kuti ine ndine Yehova.+ 22 Inu mwakhumudwitsa munthu wolungama chifukwa cha chinyengo chanu,+ pamene ineyo sindinafune kuti azivutika.* Ndipo mwalimbitsa manja a munthu woipa+ kuti asasiye njira zake zoipazo. Chifukwa cha zimenezi iye sadzapitiriza kukhala ndi moyo.+ 23 Choncho akazi inu simudzaonanso masomphenya abodza ndipo simudzaloseranso zamʼtsogolo.+ Ine ndidzapulumutsa anthu anga mʼmanja mwanu ndipo mudzadziwa kuti ine ndine Yehova.’”
14 Ndiyeno ena mwa akuluakulu a Isiraeli anabwera nʼkudzakhala pamaso panga.+ 2 Kenako Yehova anandiuza kuti: 3 “Iwe mwana wa munthu, amuna awa atsimikiza mumtima mwawo kuti azitsatira mafano awo onyansa,* ndipo aika chinthu chopunthwitsa chimene chimachititsa kuti anthu azichimwa. Kodi ndiwayankhe iwo akamandifunsa?+ 4 Choncho ulankhule nawo ndipo uwauze kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Ngati munthu aliyense mu Isiraeli watsimikiza mumtima mwake kuti azitsatira mafano ake onyansa nʼkuika chinthu chopunthwitsa chimene chachititsa kuti anthu achite tchimo kenako nʼkukafunsira kwa mneneri, ine Yehova ndidzamuyankha moyenera, mogwirizana ndi kuchuluka kwa mafano ake onyansa. 5 Ndidzachititsa mantha mitima ya anthu a nyumba ya Isiraeli,* chifukwa chakuti onsewo achoka kwa ine nʼkuyamba kutsatira mafano awo onyansawo.”’+
6 Choncho uza nyumba ya Isiraeli kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Bwererani, musiye kutsatira mafano anu onyansa ndipo musiye zinthu zonse zonyansa zimene mukuchita.+ 7 Ngati munthu aliyense amene akukhala mu Isiraeli, kaya ndi mbadwa kapena mlendo, wasiya kunditsatira ndipo watsimikiza mumtima mwake kuti azitsatira mafano ake onyansa nʼkuika chinthu chopunthwitsa chimene chachititsa kuti anthu achite tchimo kenako nʼkukafunsira kwa mneneri wanga,+ ine Yehova ndidzamuyankha ndekha. 8 Ine ndidzadana naye munthuyo nʼkumuika kuti akhale chenjezo ndi mwambi ndipo ndidzamupha kuti asakhalenso pakati pa anthu anga,+ moti mudzadziwa kuti ine ndine Yehova.”’
9 ‘Koma ngati mneneri wapusitsidwa nʼkupereka yankho, ineyo Yehova ndi amene ndapusitsa mneneriyo.+ Choncho ndidzatambasula dzanja langa nʼkumuwononga kuti asakhalenso pakati pa anthu anga, Aisiraeli. 10 Iwo adzakumana ndi zotsatira za zolakwa zawo. Zolakwa za munthu wofunsira kwa mneneri zidzakhala zofanana ndi za mneneriyo, 11 kuti a nyumba ya Isiraeli asadzasiyenso kunditsatira nʼkumangoyendayenda ndiponso kuti asiye kudziipitsa ndi zolakwa zawo zonse. Iwo adzakhala anthu anga ndipo ine ndidzakhala Mulungu wawo,’+ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”
12 Yehova anandiuzanso kuti: 13 “Iwe mwana wa munthu, ngati dziko landichimwira pochita zosakhulupirika, ine ndidzatambasula dzanja langa nʼkuwononga njira zimene amapezera chakudya.*+ Choncho ndidzatumiza njala mʼdzikolo+ ndipo ndidzapha anthu ndi ziweto.”+ 14 “‘Ngakhale amuna atatu awa: Nowa,+ Danieli+ ndi Yobu,+ akanakhala mʼdzikolo, iwo okhawo akanatha kupulumutsa miyoyo yawo chifukwa chokhala olungama,’+ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”
15 “‘Kapena nditati ndichititse zilombo zolusa zakutchire kudutsa mʼdzikolo nʼkupha anthu ambiri, nʼkulichititsa kuti likhale bwinja popanda munthu aliyense wodutsamo chifukwa cha zilombo zolusazo,+ 16 pali ine Mulungu wamoyo,’ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, ‘ngakhale zikanakhala kuti amuna atatu amenewa ali mʼdzikolo, iwo sakanapulumutsa ana awo aamuna kapena aakazi. Iwo okhawo ndi amene akanapulumuka ndipo dzikolo likanakhala bwinja.’”
17 “‘Kapena nditati ndibweretse lupanga mʼdzikolo,+ nʼkunena kuti: “Mʼdzikolo mudutse lupanga,” ine nʼkuphamo anthu ndi ziweto,+ 18 pali ine Mulungu wamoyo, akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, ‘ngakhale zikanakhala kuti amuna atatu amenewa ali mʼdzikolo, iwo sakanapulumutsa ana awo aamuna kapena aakazi. Iwo okhawo ndi amene akanapulumuka.’”
19 “‘Kapenanso ngati nditatumiza mliri mʼdzikolo,+ nʼkulikhuthulira mkwiyo wanga pokhetsa magazi ambiri komanso kupha anthu ndi ziweto, 20 pali ine Mulungu wamoyo,’ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, ‘ngakhale zikanakhala kuti Nowa,+ Danieli+ ndi Yobu+ ali mʼdzikolo, iwo sakanapulumutsa ana awo aamuna kapena aakazi. Iwo okhawo ndi amene akanapulumuka chifukwa ndi olungama.’”+
21 “Choncho Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: ‘Zidzakhalanso choncho ndikadzabweretsa zilango zanga* 4+ izi: lupanga, njala, zilombo zolusa zakutchire ndi mliri+ kuti zikaphe anthu ndi ziweto mu Yerusalemu.+ 22 Komabe anthu ena amene adzatsale mʼdzikolo adzathawa nʼkupulumuka ndipo adzatulutsidwamo,+ kuphatikizapo ana aamuna ndi aakazi. Iwo akubwera kwa inu, ndipo mukadzaona njira zawo ndi zochita zawo mudzatonthozedwa ndithu pambuyo pa tsoka limene ndinabweretsa pa Yerusalemu ndiponso pambuyo pa zonse zimene ndinachitira mzindawo.
23 Iwo adzakutonthozani mukadzaona njira zawo ndi zochita zawo. Ndipo mudzadziwa kuti zonse zimene ndinachitira mzindawo, sindinazichite popanda chifukwa,’+ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”
15 Yehova analankhulanso nane kuti: 2 “Iwe mwana wa munthu, kodi mtengo wa mpesa umasiyana bwanji ndi mitengo ina yonse kapena nthambi ya mitengo yamʼnkhalango? 3 Kodi anthu amadula nthambi yake kuti ikhale mtengo wogwiritsa ntchito inayake? Kapena kodi angatenge kamtengo kake nʼkukakhomerera pakhoma kuti azikolowekapo ziwiya zosiyanasiyana? 4 Mtengowo umaponyedwa pamoto kuti ukhale nkhuni ndipo motowo umanyeketsa kutsinde ndi kunsonga kwake. Pakati pa mtengowo pamapsanso. Ndiye kodi ungagwire ntchito iliyonse? 5 Ngakhale pamene mtengowo unali wathunthu sukanagwiritsidwa ntchito iliyonse. Ndiye kuli bwanji ukapsa ndi moto nʼkunyeka, kodi ungagwirenso ntchito iliyonse?”
6 “Choncho Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: ‘Mofanana ndi mtengo wa mpesa womwe uli pakati pa mitengo yamʼnkhalango, umene ndaupereka kuti ukhale nkhuni, ndidzachitanso chimodzimodzi ndi anthu amene akukhala mu Yerusalemu.+ 7 Anthuwo ndawayangʼana mokwiya. Iwo athawa moto, koma moto wina udzawapsereza. Ndipo ndikadzawayangʼana mokwiya, mudzadziwa kuti ine ndine Yehova.+
8 Dziko lawo ndidzalisandutsa bwinja+ chifukwa chakuti iwo achita zosakhulupirika,’+ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”
16 Yehova analankhulanso nane kuti: 2 “Iwe mwana wa munthu, uza Yerusalemu zinthu zake zonyansa zimene akuchita.+ 3 Umuuze kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, akuuza iwe Yerusalemu kuti: “Iwe unachokera kudziko la Akanani ndipo unabadwira komweko. Bambo ako anali a Chiamori+ ndipo mayi ako anali Muhiti.+ 4 Pa tsiku limene unabadwa, mchombo wako sunadulidwe. Sanakusambitse kuti ukhale woyera, sanakupake mchere ndipo sanakukulunge munsalu. 5 Palibe amene anakumvera chisoni kuti akuchitire chilichonse mwa zinthu zimenezi. Palibe amene anakuchitira chifundo. Mʼmalomwake anakutaya patchire chifukwa anthu anadana nawe pa tsiku limene unabadwa.
6 Ine ndikudutsa pafupi ndinakuona ukuponyaponya timiyendo tako mʼmwamba uli magazi okhaokha. Ndiyeno utagona pansi ndiponso uli ndi magazi okhaokha ndinakuuza kuti, ‘Ukhala ndi moyo!’ Ndithu ndinakuuza uli magazi okhaokha kuti, ‘Ukhala ndi moyo!’ 7 Ndinakupangitsa kuti ukhale gulu lalikulu la anthu ngati mbewu zimene zaphuka mʼmunda. Unakula nʼkukhala mtsikana ndipo unkavala zodzikongoletsera zabwino kwambiri. Mabere ako anakula ndipo tsitsi lako linatalika, koma unali udakali wosavala ndiponso wamaliseche.”’
8 ‘Ndikudutsa pafupi ndinakuona ndipo ndinazindikira kuti wafika pamsinkhu woti utha kuyamba kukondana ndi munthu. Choncho ndinakuphimba ndi chovala changa+ ndipo ndinabisa maliseche ako. Ndinalumbira nʼkuchita nawe pangano ndipo unakhala wanga,’ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. 9 ‘Komanso ndinakusambitsa ndipo ndinatsuka magazi ako nʼkukudzoza mafuta.+ 10 Kenako ndinakuveka chovala cha nsalu yopeta ndi nsapato za chikopa chabwino kwambiri.* Ndinakukulunga munsalu zabwino kwambiri nʼkukuveka zovala zamtengo wapatali. 11 Ndinakuvekanso zokongoletsera komanso ndinakuveka zibangili mʼmanja mwako ndi mkanda mʼkhosi mwako. 12 Ndinakuvekanso ndolo yapamphuno ndi ndolo zamʼmakutu ndiponso chisoti chokongola pamutu pako. 13 Unapitiriza kudzikongoletsa ndi zinthu zagolide ndi zasiliva. Zovala zako zinali za nsalu zabwino kwambiri, nsalu zamtengo wapatali komanso chovala cha nsalu yopeta. Unkadya ufa wosalala, uchi ndi mafuta ndipo unakhala wokongola kwambiri+ moti unali woyenera kukhala mfumukazi.*
14 Unatchuka* kwambiri pakati pa mitundu ya anthu+ chifukwa cha kukongola kwako. Zili choncho chifukwa kukongola kwako kunali kogometsa popeza ndinaika ulemerero wanga pa iwe,’+ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.
15 ‘Koma unayamba kudalira kukongola kwako+ ndipo unakhala hule chifukwa cha kutchuka kwako.+ Unayamba kuchita uhule mosadziletsa ndi munthu aliyense wodutsa mʼnjira+ ndipo unapereka kukongola kwako kwa anthu odutsawo. 16 Unatenga zovala zako zina za mitundu yosiyanasiyana nʼkukongoletsera malo okwezeka pamene unkachitirapo uhule.+ Zinthu zimene siziyenera kuchitika ndipo zisadzachitikenso. 17 Unatenganso zinthu zako zodzikongoletsera zagolide ndi zasiliva zimene ndinakupatsa ndipo unapangira zifaniziro za munthu wamwamuna nʼkumachita nazo uhule.+ 18 Unatenga zovala zako za nsalu yopeta nʼkuphimbira zifanizirozo ndipo unapereka mafuta anga ndi zonunkhiritsa zanga kwa zifanizirozo.+ 19 Komanso buledi amene ndinakupatsa kuti udye, wopangidwa ndi ufa wosalala, mafuta ndi uchi, unamuperekanso kwa zifanizirozo kuti zikhale kafungo kosangalatsa.*+ Izi ndi zimene zinachitikadi,’ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.
20 ‘Unatenga ana ako aamuna ndi aakazi amene unandiberekera+ nʼkuwapereka nsembe kwa mafano.+ Kodi zochita zako zauhulezo sizinakukwanire? 21 Unapha ana anga ndipo unawapereka nsembe powaponya pamoto.+ 22 Pamene unkachita zinthu zako zonse zonyansa komanso zauhulezo, sunakumbukire zimene ndinakuchitira uli wakhanda pamene unali wamaliseche komanso wosavala, ukuponyaponya timiyendo tako mʼmwamba ndiponso uli magazi okhaokha. 23 Tsoka, tsoka kwa iwe chifukwa unachita zinthu zoipa zonsezi!’+ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. 24 ‘Unamanga malo oti uzilambirirapo milungu yabodza ndipo unakonza malo okwera mʼbwalo lililonse la mzinda. 25 Unamanga malo ako okwerawo pamalo oonekera bwino kwambiri mumsewu uliwonse ndipo kukongola kwako unakusandutsa chinthu chonyansa podzipereka kwa munthu* aliyense wodutsa+ ndipo unachulukitsa zochita zako zauhulezo.+ 26 Unachita uhule ndi ana aamuna a Iguputo,+ anthu oyandikana nawo amene ali ndi chilakolako champhamvu chogonana,* ndipo unandikhumudwitsa ndi zochita zako zauhule zosawerengeka. 27 Tsopano ine nditambasula dzanja langa nʼkukulanga ndipo ndichepetsa chakudya chimene ndimakupatsa.+ Ndikupereka kwa akazi amene amadana nawe+ kuti achite nawe zimene akufuna. Ndikupereka kwa ana aakazi a Afilisiti, amene ankanyansidwa ndi khalidwe lako lonyansa.+
28 Chifukwa chosakhutira, unachitanso uhule ndi ana aamuna a Asuri.+ Koma utachita uhule ndi amuna amenewa sunakhutirebe. 29 Choncho unawonjezera kuchita zauhule ndi dziko la anthu a malonda* ndiponso Akasidi.+ Koma ngakhale unachita zimenezo sunakhutirebe. 30 Mtima wako unali wofooka kwambiri pamene unkachita zinthu zonsezi.* Wakhala ukuchita zinthu ngati hule lopanda manyazi!’ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.+ 31 ‘Koma pamene unamanga malo oti uzilambirirapo milungu yabodza, pamalo oonekera bwino kwambiri mumsewu uliwonse komanso kukonza malo okwera mʼbwalo lililonse la mzinda, sunali ngati hule chifukwa unkakana kulipidwa. 32 Ndiwe mkazi wachigololo amene ukukonda amuna achilendo mʼmalo mwa mwamuna wako.+ 33 Anthu amapereka mphatso kwa mahule onse,+ koma iweyo ndi amene wapereka mphatso kwa zibwenzi zako zonse.+ Umawapatsa ziphuphu kuti abwere kwa iwe kuchokera kumalo onse ozungulira kuti adzachite nawe zauhule.+ 34 Iweyo umachita zosiyana ndi akazi ena amene amachita uhule. Palibe amene amachita uhule ngati mmene iwe umachitira. Iweyo ndi amene umapereka malipiro kwa amuna koma iwowo sakulipira. Zimene umachita nʼzosiyana ndi zimene mahule ena amachita.’
35 Choncho hule iwe,+ imva mawu a Yehova. 36 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: ‘Chifukwa wasonyeza chilakolako mopitirira muyezo ndipo maliseche ako aonekera pamene umachita zauhule ndi zibwenzi zako ndiponso mafano ako onse onyansa,*+ amene unafika powapatsa nsembe za magazi a ana ako,+ 37 ine ndikusonkhanitsa pamodzi zibwenzi zako zonse zimene unkazisangalatsa, onse amene unkawakonda limodzi ndi onse amene unkadana nawo. Ndidzawasonkhanitsa pamodzi kuchokera kumadera onse ozungulira kuti akuukire ndipo ndidzakuvula kuti aone maliseche ako, moti adzakuona uli mbulanda.+
38 Ndidzakupatsa chiweruzo chimene chimayenera kuperekedwa kwa akazi achigololo+ ndi kwa akazi okhetsa magazi+ ndipo magazi ako adzakhetsedwa mokwiya komanso mwansanje.+ 39 Ndidzakupereka mʼmanja mwa anthu okuukira ndipo iwo adzagwetsa malo ako olambirirako milungu yabodza ndi malo ako okwera.+ Iwo adzakuvula zovala+ ndipo adzatenga zinthu zako zodzikongoletsera zamtengo wapatali+ nʼkukusiya wosavala komanso wamaliseche. 40 Adzakubweretsera chigulu cha anthu+ kuti chikuukire. Iwo adzakugenda ndi miyala+ ndipo adzakupha ndi malupanga awo.+ 41 Iwo adzawotcha nyumba zako ndi moto+ ndipo adzakulanga pamaso pa akazi ambiri. Ndidzathetsa uhule wako+ ndipo udzasiya kupereka malipiro. 42 Mkwiyo wanga ndidzauthetsera pa iwe+ moti sindidzakukwiyiranso.+ Ndidzangokhala osachita kalikonse ndipo sindidzakhalanso wokwiya.’
43 ‘Chifukwa sunakumbukire zimene ndinakuchitira uli wakhanda+ ndipo wandikwiyitsa pochita zinthu zonsezi, tsopano ndikubwezera mogwirizana ndi zochita zako. Ndipo sudzapitirizanso kuchita khalidwe lako lonyansa komanso zinthu zonse zonyansa zimene ukuchita,’ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.
44 ‘Aliyense amene amanena miyambi adzakunenera mwambi wakuti, “Make mbuu, mwana mbuu!”+ 45 Iweyo uli ngati mayi ako, amene ankanyansidwa ndi mwamuna wawo komanso ana awo. Ulinso ngati azichemwali ako amene ankanyansidwa ndi amuna awo ndi ana awo. Mayi ako anali Muhiti ndipo bambo ako anali a Chiamori.+
46 Mkulu wako ndi Samariya+ amene akukhala kumpoto kwako* limodzi ndi ana ake aakazi.*+ Ndipo mngʼono wako ndi Sodomu,+ amene akukhala kumʼmwera kwako* limodzi ndi ana ake aakazi.+ 47 Iwe sikuti unangoyenda mʼnjira zawo ndiponso sikuti unkangotsatira zinthu zawo zonyansa zimene ankachita basi, koma mʼkanthawi kochepa zochita zako zonse zinakhala zoipa kwambiri kuposa zimene iwowo ankachita.+ 48 Pali ine Mulungu wamoyo, mchemwali wako Sodomu ndi ana ake aakazi, sanachite zofanana ndi zimene iwe ndi ana ako aakazi mwachita,’ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. 49 ‘Tamvera! Zolakwa za mchemwali wako Sodomu zinali izi: Iye ndi ana ake aakazi+ anali onyada,+ anali ndi chakudya chochuluka+ komanso ankakhala moyo wabata ndi wosatekeseka,+ koma sankathandiza anthu ovutika ndi osauka.+ 50 Iwo anapitiriza kudzikweza+ komanso kuchita zinthu zonyansa pamaso panga.+ Choncho ndinaona kuti nʼzoyenera kuti ndiwawononge.+
51 Komanso Samariya+ sanachite machimo ofika ngakhale hafu ya machimo ako. Koma iwe unapitiriza kuchulukitsa zinthu zonyansa zimene unkachita kuposa abale ako, moti unachititsa kuti azichemwali ako aoneke ngati olungama chifukwa cha zinthu zonse zonyansa zimene unkachita.+ 52 Tsopano iweyo ukuyenera kuchita manyazi chifukwa waikira kumbuyo makhalidwe a azichemwali ako. Iwowo ndi olungama kuposa iweyo chifukwa cha tchimo lako lochita zinthu zonyansa kwambiri kuposa zimene iwowo anachita. Choncho uchite manyazi ndi kunyozeka chifukwa chakuti wachititsa kuti azichemwali ako aoneke ngati olungama.’
53 ‘Ine ndidzasonkhanitsa anthu awo amene anatengedwa kupita kudziko lina. Ndidzasonkhanitsa anthu a ku Sodomu ndi ana ake aakazi amene anagwidwa komanso anthu a ku Samariya ndi ana ake aakazi amene anagwidwa. Posonkhanitsa anthu amenewa ndidzasonkhanitsanso anthu ako amene anatengedwa kupita ku dziko lina,+ 54 kuti udzachite manyazi. Iwe udzachita manyazi chifukwa cha zimene wachita powatonthoza. 55 Azichemwali ako, omwe ndi Sodomu ndi ana ake aakazi ndiponso Samariya ndi ana ake aakazi, adzakhalanso ngati mmene analili kale. Komanso iweyo ndi ana ako aakazi mudzakhalanso ngati mmene munalili kale.+ 56 Mchemwali wako Sodomu sunkamuona kuti ndi woyenera kumutchula mʼmasiku amene unkanyada, 57 zoipa zako zisanaonekere.+ Koma pano ana aakazi a Siriya ndi anthu oyandikana naye akukunyoza komanso ana aakazi a Afilisiti+ ndi onse amene akuzungulira akukuchitira zachipongwe. 58 Udzakumana ndi zotsatira za khalidwe lako lonyansa ndiponso zinthu zonyansa zimene ukuchita,’ akutero Yehova.
59 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: ‘Tsopano ndikulanga mogwirizana ndi zochita zako,+ chifukwa unanyoza lumbiro pophwanya pangano langa.+ 60 Koma ine ndidzakumbukira pangano limene ndinapangana nawe uli wakhanda ndipo ndidzachita nawe pangano limene lidzakhalepo mpaka kalekale.+ 61 Udzakumbukira khalidwe lako ndipo udzachita manyazi+ ukadzalandira azichemwali ako omwe ndi akulu ako komanso angʼono ako. Ndidzawapereka kwa iwe kuti akhale ana ako aakazi, koma osati chifukwa cha pangano limene ndinachita ndi iwe.
62 Ineyo ndidzachita pangano ndi iwe ndipo udzadziwa kuti ine ndine Yehova. 63 Kenako udzakumbukira ndipo udzachita manyazi kwambiri moti sudzatha kutsegula pakamwa pako chifukwa cha manyaziwo,+ ndikadzaphimba machimo ako ngakhale kuti unachita zonsezi,’+ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”
17 Yehova analankhulanso nane kuti: 2 “Iwe mwana wa munthu, nena mawu ophiphiritsa komanso mwambi wokhudza nyumba ya Isiraeli.+ 3 Unene kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Ku Lebanoni+ kunabwera chiwombankhanga chachikulu+ cha mapiko akuluakulu komanso ataliatali. Chiwombankhangacho chinali ndi nthenga zambiri zamitundu yosiyanasiyana. Chitafika kumeneko, chinathyola nsonga ya mtengo wa mkungudza.+ 4 Chiwombankhangacho chinathyola nsonga yapamwamba penipeni pa nthambi za mtengowo nʼkupita nayo kudziko la anthu ochita malonda.* Kumeneko chinakadzala nsonga ya mkungudzayo mumzinda umene munali anthu ochita malonda.+ 5 Kenako chinatenga mbewu imodzi mwa mbewu zamʼdzikomo+ nʼkuidzala mʼmunda wachonde. Chinadzala mbewuyo mʼmphepete mwa madzi ambiri kuti ikule ngati mtengo wa msondodzi. 6 Mbewuyo inamera nʼkukhala mtengo wa mpesa+ waufupi wamasamba ambiri. Nthambi za mtengowo sizinkakulira mʼmbali ndipo mizu yake inali pansi pa nthambizo. Choncho mbewuyo inakhala mtengo wa mpesa ndipo inaphuka nʼkuchita nthambi.+
7 Kenako kunabwera chiwombankhanga china chachikulu+ chamapiko akuluakulu komanso nthenga zikuluzikulu.+ Ndiyeno mwamsanga, mtengo wa mpesawo unatambasula mizu yake kupita kumene kunali chiwombankhangacho kutali ndi malo amene unadzalidwa. Mtengo wa mpesawo unatambasula nthambi zake kukafika pamene panali chiwombankhangacho kuti chiuthirire.+ 8 Koma mtengowo anali ataudzala kale mʼmunda wabwino pafupi ndi madzi ambiri, kuti uchite nthambi, ubereke zipatso nʼkukhala mtengo waukulu wa mpesa.”’+
9 Ndiyeno unene kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Kodi mtengo umenewu zinthu zidzauyendera bwino? Kodi munthu wina sadzadula mizu yake+ nʼkuchititsa kuti zipatso zake ziwole komanso kuchititsa kuti mphukira zake zinyale?+ Mtengowo udzauma kwambiri moti sipadzachita kufunika dzanja lamphamvu kapena anthu ambiri kuti auzule ndi mizu yomwe. 10 Ngakhale kuti mtengowo anautenga pamalo ena nʼkukaudzala pamalo ena, kodi zinthu zidzauyendera bwino? Kodi sudzaumiratu ukadzawombedwa ndi mphepo yakumʼmawa? Mtengowo udzauma pamalo amene unadzalidwapo.”’”
11 Yehova analankhulanso nane kuti: 12 “Chonde, uza anthu opandukawo kuti, ‘Kodi simukuzindikira tanthauzo la zinthu zimenezi?’ Auze kuti, ‘Mfumu ya Babulo inabwera ku Yerusalemu nʼkudzatenga mfumu ndi akalonga amumzindawo nʼkupita nawo ku Babulo.+ 13 Kuwonjezera apo, inatenga mmodzi mwa ana* achifumu+ nʼkuchita naye pangano ndi kumulumbiritsa.+ Kenako mfumuyo inatenga anthu otchuka amʼdzikolo nʼkupita nawo kwawo+ 14 nʼcholinga choti ufumuwo ukhale waungʼono, usakhalenso wamphamvu, koma kuti ufumuwo udzapitirize kukhalapo ngati Aisiraeli atasunga pangano limene anachita.+ 15 Koma kenako mfumu ya Yuda inapandukira mfumu ya Babulo+ potumiza amithenga ku Iguputo kuti akatenge mahatchi+ ndi gulu lalikulu la asilikali.+ Kodi zinthu zidzaiyendera bwino? Kodi munthu amene akuchita zinthu zimenezi angapewe chilango? Kodi angaphwanye pangano nʼkupewabe chilango?’+
16 ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, “Pali ine Mulungu wamoyo, munthu amene ananyoza lumbiro ndi kuphwanya pangano limene anachita ndi mfumu* imene inamulonga* ufumu, adzafera mʼdziko la Babulo, kumene mfumuyo imakhala.+ 17 Gulu lalikulu la asilikali komanso asilikali ambirimbiri a Farao sadzamuthandiza pankhondo,+ adani akadzamanga malo okwera omenyerapo nkhondo ndiponso mpanda womenyerapo nkhondo nʼcholinga chakuti aphe anthu ambiri. 18 Iye wanyoza lumbiro limenelo komanso waphwanya pangano. Ngakhale kuti analonjeza,* iye wachita zinthu zonsezi ndipo sadzapulumuka.”’
19 ‘Choncho Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Pali ine Mulungu wamoyo, ndidzamulanga chifukwa chonyoza lumbiro langa+ ndiponso chifukwa chophwanya pangano langa. 20 Ndidzamuponyera ukonde wanga ndipo adzakodwa mu ukonde wanga wosakira.+ Ndiyeno ndidzamubweretsa ku Babulo nʼkumuweruza chifukwa chondichitira zinthu mosakhulupirika.+ 21 Asilikali ake onse amene anathawa adzaphedwa ndi lupanga ndipo amene adzapulumuke adzabalalikira kumbali zonse.*+ Zikadzatero mudzadziwa kuti ine Yehova ndi amene ndanena zimenezi.”’+
22 ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Ine ndidzathyola nsonga yapamwamba penipeni pa mtengo wa mkungudza+ nʼkuidzala. Ndidzabudula mphukira yanthete pamwamba pa nsonga zake+ ndipo ndidzaidzala pamwamba pa phiri lalitali kwambiri.+ 23 Ndidzaidzala pamwamba pa phiri lalitali la ku Isiraeli. Nthambi zake zidzakula ndipo udzabereka zipatso nʼkukhala mtengo waukulu wa mkungudza. Mbalame zamitundu yonse zizidzakhala pansi pa mtengowo ndi mumthunzi wa masamba ake. 24 Mitengo yonse yamʼthengo idzadziwa kuti ine Yehova ndatsitsa mtengo waukulu nʼkukweza mtengo wonyozeka.+ Idzadziwa kuti ndaumitsa mtengo wauwisi nʼkuchititsa maluwa mtengo umene unali wouma.+ Ine Yehova ndanena komanso kuchita zimenezi.”’”
18 Yehova analankhulanso nane kuti: 2 “Kodi mwambi umene mumanena mʼdziko la Isiraeli wakuti, ‘Bambo adya mphesa zosapsa koma mano a ana ndi amene ayezimira,’+ umatanthauza chiyani?
3 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Pali ine Mulungu wamoyo, simudzanenanso mwambi umenewu mu Isiraeli. 4 Tamverani! Miyoyo yonse ndi yanga. Moyo wa bambo komanso moyo wa mwana, yonse ndi yanga. Moyo umene wachimwa ndi umene udzafe.*
5 Tiyerekeze kuti munthu ndi wolungama ndipo amachita zinthu motsatira malamulo ndiponso mwachilungamo. 6 Iye sadya zinthu zoperekedwa nsembe kwa mafano mʼmapiri+ komanso sadalira mafano onyansa* a nyumba ya Isiraeli. Iye sagona ndi mkazi wa mnzake+ kapena kugona ndi mkazi amene akusamba.+ 7 Sazunza munthu aliyense+ koma amabweza chikole kwa munthu amene anakongola zinthu zake.+ Salanda zinthu za ena mwauchifwamba+ koma amapereka chakudya chake kwa munthu amene ali ndi njala+ ndiponso amaphimba munthu wamaliseche ndi chovala.+ 8 Iye sauza anthu kuti amupatse chiwongoladzanja akabwereketsa zinthu ndipo sakongoza zinthu mwa katapira+ koma amapewa kuchita zinthu mopanda chilungamo.+ Iye amatsatira chilungamo chenicheni akamaweruza munthu ndi mnzake.+ 9 Ndipo amapitiriza kuyenda motsatira malamulo anga ndi kusunga zigamulo zanga kuti azichita zinthu mokhulupirika. Munthu ameneyu ndi wolungama, ndithu adzapitiriza kukhala ndi moyo,’+ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.
10 ‘Koma ngati munthuyo wabereka mwana wamwamuna, mwanayo nʼkukhala wakuba+ kapena wopha anthu+ kapenanso amachita chilichonse cha zinthu zimenezi, 11 (ngakhale kuti bamboyo sanachitepo chilichonse mwa zinthu zimenezi), ngati mwanayo amadya chakudya choperekedwa nsembe kwa mafano mʼmapiri ndipo amagona ndi mkazi wa mnzake, 12 ngati amazunza munthu wovutika ndi wosauka,+ ngati amalanda zinthu za ena mwauchifwamba, ngati sabweza chikole, ngati amadalira mafano onyansa,+ ngati amachita makhalidwe onyansa,+ 13 ngati amakongoza zinthu zake mwa katapira ndipo amauza anthu kuti apereke chiwongoladzanja,+ ndiye kuti mwanayo sadzapitiriza kukhala ndi moyo. Chifukwa wachita zinthu zonyansa zonsezi, iye adzaphedwa ndithu. Magazi ake adzakhala pamutu pake.
14 Koma tiyerekeze kuti bambo ali ndi mwana wamwamuna amene amaona machimo onse amene bambo akewo amachita. Ngakhale kuti mwanayo amaona bambo ake akuchita machimowo, iye sachita nawo. 15 Iye sadya chakudya choperekedwa nsembe kwa mafano mʼmapiri. Sadalira mafano onyansa a nyumba ya Isiraeli ndipo sagona ndi mkazi wa mnzake. 16 Sazunza munthu aliyense. Satenga chikole ndipo salanda chilichonse mwauchifwamba. Munthu wanjala amamupatsa chakudya ndipo munthu wamaliseche amamuphimba ndi chovala. 17 Iye amapewa kupondereza munthu wosauka, sakongoza zinthu mwa katapira ndipo sauza anthu kuti apereke chiwongoladzanja. Amatsatira zigamulo zanga komanso kuyenda motsatira malamulo anga. Munthu wotere sadzafa chifukwa cha zolakwa za bambo ake. Iye adzapitiriza kukhala ndi moyo ndithu. 18 Koma popeza kuti bambo akewo ankachita zachinyengo, ankabera mʼbale wawo mwauchifwamba ndipo ankachita zinthu zoipa pakati pa anthu a mtundu wawo, iwo adzafa chifukwa cha zolakwa zawo.
19 Koma mudzanena kuti: “Nʼchifukwa chiyani mwanayo alibe mlandu uliwonse pa zolakwa za bambo akewo?” Popeza kuti mwanayo anachita zinthu motsatira malamulo ndiponso mwachilungamo, anasunga malamulo anga onse komanso kuwatsatira, ndithu iye adzapitiriza kukhala ndi moyo.+ 20 Moyo umene ukuchimwawo ndi umene udzafe.*+ Mwana sadzakhala ndi mlandu uliwonse pa zolakwa za bambo ake ndipo bambo sadzakhala ndi mlandu uliwonse pa zolakwa za mwana wake. Munthu wolungama adzaweruzidwa yekha mogwirizana ndi zinthu zachilungamo zimene amachita, ndipo munthu woipa adzaweruzidwa yekha mogwirizana ndi zinthu zoipa zimene amachita.+
21 Koma ngati munthu woipa wasiya kuchita machimo ake onse amene ankachita ndipo akusunga malamulo anga nʼkumachita zinthu motsatira malamulo ndiponso mwachilungamo, ndithu iye adzapitiriza kukhala ndi moyo. Sadzafa ayi.+ 22 Iye sadzalangidwa chifukwa cha zolakwa zonse zimene anachita.*+ Adzapitiriza kukhala ndi moyo chifukwa chochita zinthu zolungama.’+
23 ‘Kodi ine ndimasangalala ndi imfa ya munthu wochimwa?+ Kodi zimene ine ndimafuna si zoti munthu wochimwayo alape nʼkupitiriza kukhala ndi moyo?’+ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.
24 ‘Munthu amene amachita zinthu zabwino akasiya kuchita zabwinozo nʼkumachita zoipa,* akamachita zinthu zonse zonyansa zimene munthu woipa amachita, kodi angapitirize kukhala ndi moyo? Zinthu zabwino zimene ankachita sizidzakumbukiridwa.+ Iye adzafa chifukwa chochita zinthu mosakhulupirika ndiponso chifukwa cha machimo ake amene anachita.+
25 Koma inu mudzanena kuti: “Njira za Yehova nʼzopanda chilungamo.”+ Tamverani inu a nyumba ya Isiraeli. Kodi njira zanga nʼzimene zili zopanda chilungamo?+ Kodi njira zanu si zimene zili zopanda chilungamo?+
26 Munthu amene amachita zinthu zabwino akasiya kuchita zabwinozo nʼkumachita zoipa,* nʼkufa chifukwa cha zochita zakezo, adzakhala kuti wafa chifukwa cha zoipa zake.
27 Ndipo ngati munthu woipa wasiya kuchita zinthu zoipa zimene ankachita nʼkuyamba kuchita zinthu motsatira malamulo ndiponso mwachilungamo, iye adzapulumutsa moyo wake.+ 28 Munthu woipayo akazindikira kuti zimene akuchita ndi zoipa nʼkusiya kuchita zoipazo, ndithu iye adzapitiriza kukhala ndi moyo. Sadzafa ayi.
29 Koma nyumba ya Isiraeli idzanena kuti: “Njira za Yehova nʼzopanda chilungamo.” Kodi nʼzoona kuti njira zanga nʼzimene zili zopanda chilungamo, inu a nyumba ya Isiraeli?+ Kodi njira zanu si zimene zili zopanda chilungamo?’
30 ‘Choncho ine ndidzaweruza aliyense wa inu mogwirizana ndi njira zake,+ inu a nyumba ya Isiraeli,’ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. ‘Lapani ndipo musiyiretu zolakwa zanu zonse kuti zisakhale chinthu chokupunthwitsani chimene chingachititse kuti mukhale ndi mlandu. 31 Siyani zolakwa zanu zonse zimene munkachita+ ndipo mukhale ndi mtima watsopano* komanso mzimu watsopano.+ Kodi muferenji+ inu a nyumba ya Isiraeli?’
32 ‘Inetu sindisangalala ndi imfa ya munthu aliyense,’+ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. ‘Choncho siyani kuchita zoipa kuti mupitirize kukhala ndi moyo.’”+
19 “Ukuyenera kuimba nyimbo yoimba polira yokhudza atsogoleri a Isiraeli. 2 Unene kuti,
‘Kodi mayi anu anali ngati ndani? Anali ngati mkango waukazi pakati pa mikango ina.
Ankagona pakati pa mikango yamphamvu,* nʼkumalera ana ake.
3 Mkangowo unalera mwana wake wina ndipo mwanayo anakula nʼkukhala mkango wamphamvu.+
Anaphunzira kupha nyama
Ndipo anayamba kudya ngakhale anthu.
4 Mitundu ya anthu inamva za mwana wa mkangoyo ndipo inakumba dzenje limene anagweramo,
Kenako anamukola ndi ngowe nʼkupita naye ku Iguputo.+
5 Mkango waukazi uja unadikira koma patapita nthawi unaona kuti palibe chiyembekezo chakuti mwanayo adzabwereranso.
Choncho unatenga mwana wake wina nʼkumutumiza ngati mkango wamphamvu.
6 Mkangowo unayambanso kuyendayenda pakati pa mikango ina ndipo unakhala mkango wamphamvu.
Unaphunzira kupha nyama ndipo unayamba kudya ngakhale anthu.+
7 Mkangowo unkasaka nyama pakati pa nsanja zawo zokhala ndi mipanda yolimba ndipo unawononga mizinda yawo.
Moti mʼdziko labwinjalo munkangomveka kubangula kwa mkangowo.+
8 Mitundu ya anthu imene inkakhala mʼzigawo zozungulira inabwera kudzauukira ndipo inautchera ukonde,
Mkangowo unagwera mʼdzenje lawo.
9 Kenako anaukola ndi ngowe nʼkuuika mʼkakhola ndipo anapita nawo kwa mfumu ya Babulo.
Atafika nawo anautsekera kuti mawu ake asadzamvekenso mʼmapiri a ku Isiraeli.
10 Mayi anu anali ngati mtengo wa mpesa*+ umene unadzalidwa mʼmphepete mwa madzi.
Mtengowo unabereka zipatso ndipo unali ndi nthambi zambiri chifukwa unali pamadzi ambiri.
11 Nthambi* za mtengowo zinakhala zolimba, zoyenera kupangira ndodo za olamulira.
Mtengowo unakula nʼkutalika kwambiri kuposa mitengo ina,
Ndipo unkaonekera patali chifukwa cha kutalika kwake ndiponso kuchuluka kwa masamba ake.
12 Koma mtengowo unazulidwa mwaukali+ nʼkuponyedwa pansi,
Ndipo mphepo yakumʼmawa inaumitsa zipatso zake.
Nthambi zake zimene zinali zolimba zinathyoledwa nʼkuuma+ ndipo zinawotchedwa ndi moto.+
14 Motowo unafalikira kuchokera kunthambi* zake ndipo unawotcha mphukira ndi zipatso zake,
Ndipo mtengowo unalibenso nthambi zolimba komanso ndodo ya olamulira.+
Imeneyi ndi nyimbo yoimba polira ndipo idzakhala nyimbo yotchuka.’”
20 Mʼchaka cha 7, mʼmwezi wa 5, pa tsiku la 10 la mweziwo, akuluakulu ena a Isiraeli anabwera nʼkudzakhala pansi pafupi ndi ine kuti adzafunsire kwa Yehova. 2 Ndiyeno Yehova anandiuza kuti: 3 “Iwe mwana wa munthu, lankhula ndi akuluakulu a Isiraeliwo ndipo uwauze kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Kodi mwabwera kudzafunsira kwa ine? ‘Pali ine Mulungu wamoyo, sindikuyankhani,’+ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”’
4 Kodi wakonzeka kuti uwaweruze? Kodi wakonzeka kuwaweruza, iwe mwana wa munthu? Auze zinthu zonyansa zimene makolo awo anachita.+ 5 Uwauze kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Pa tsiku limene ndinasankha Isiraeli,+ ndinalumbiranso* kwa ana* a Yakobo ndipo ndinawachititsa kuti andidziwe mʼdziko la Iguputo.+ Inde, ndinalumbira kwa iwo nʼkunena kuti, ‘Ine ndine Yehova Mulungu wanu.’ 6 Pa tsiku limenelo ndinalumbira kuti ndidzawatulutsa mʼdziko la Iguputo nʼkupita nawo kudziko limene ndinawasankhira,* dziko loyenda mkaka ndi uchi.+ Linali dziko lokongola kwambiri kuposa mayiko onse. 7 Kenako ndinawauza kuti, ‘Aliyense wa inu ataye zinthu zonyansa zimene akuzitumikira. Musadziipitse ndi mafano onyansa* a ku Iguputo.+ Ine ndine Yehova Mulungu wanu.’+
8 Koma iwo anandipandukira ndipo sanafune kundimvera. Iwo sanataye zinthu zonyansa zimene ankazitumikira ndipo sanasiye kulambira mafano onyansa a ku Iguputo.+ Choncho ine ndinatsimikiza mtima kuti ndiwatsanulire mkwiyo wanga komanso kuwaonetsa ukali wanga wonse mʼdziko la Iguputo. 9 Koma ndinachitapo kanthu chifukwa cha dzina langa kuti lisadetsedwe pamaso pa anthu a mitundu ina kumene ankakhalako.+ Chifukwa ndinachititsa kuti iwo* andidziwe pamaso pa anthu a mitundu inawo pamene ndinawatulutsa* mʼdziko la Iguputo.+ 10 Choncho ndinawatulutsa mʼdziko la Iguputo nʼkuwalowetsa mʼchipululu.+
11 Kenako ndinawapatsa malamulo anga ndi kuwadziwitsa zigamulo zanga+ kuti munthu amene akuzitsatira akhale ndi moyo.+ 12 Ndinawapatsanso sabata langa+ kuti likhale chizindikiro pakati pa ine ndi iwowo.+ Ndinachita zimenezi nʼcholinga choti adziwe kuti ine Yehova, ndi amene ndikuwachititsa kuti akhale opatulika.
13 Koma a nyumba ya Isiraeli anandipandukira mʼchipululu.+ Iwo sanatsatire malamulo anga ndipo anakana zigamulo zanga zimene munthu akamazitsatira, zimamuthandiza kuti akhale ndi moyo. Sabata langa analidetsa kwambiri. Choncho ndinatsimikiza mtima kuti ndiwatsanulire mkwiyo wanga mʼchipululu kuti onse ndiwawonongeretu.+ 14 Ndinachitapo kanthu chifukwa cha dzina langa kuti lisadetsedwe pamaso pa anthu a mitundu ina amene anaona ndikutulutsa anthu anga pakati pawo.+ 15 Ndinalumbiranso kwa iwo mʼchipululu kuti sindidzawalowetsa mʼdziko limene ndinawapatsa,+ dziko loyenda mkaka ndi uchi+ komanso lokongola kwambiri kuposa mayiko onse. 16 Ndinachita zimenezi chifukwa anakana zigamulo zanga, sanatsatire malamulo anga ndipo anadetsa sabata langa popeza anatsimikiza mtima kuti azilambira mafano awo onyansa.+
17 Koma ndinawamvera chisoni ndipo sindinawawononge. Sindinawaphe onse mʼchipululu. 18 Ndinauza ana awo mʼchipululu+ kuti, ‘Musamatsatire malamulo a makolo anu+ kapena kusunga zigamulo zawo kapenanso kudziipitsa ndi mafano awo onyansa. 19 Ine ndine Yehova Mulungu wanu. Muzitsatira malamulo anga ndipo muzisunga zigamulo zanga komanso kuzitsatira.+ 20 Muzisunga sabata langa kuti likhale lopatulika+ ndipo lidzakhala chizindikiro pakati pa ine ndi inu, kuti mudziwe kuti ine ndine Yehova Mulungu wanu.’+
21 Koma anawo anayamba kundipandukira.+ Sanatsatire malamulo anga ndipo sanasunge komanso kutsatira zigamulo zanga, zimene ngati munthu atazitsatira zingamuthandize kuti akhale ndi moyo. Iwo anadetsa sabata langa. Choncho ine ndinatsimikiza mtima kuti ndiwatsanulire mkwiyo wanga komanso kuwaonetsa ukali wanga wonse mʼchipululu.+ 22 Koma sindinatero+ ndipo ndinachitapo kanthu chifukwa cha dzina langa+ kuti lisadetsedwe pamaso pa anthu a mitundu ina amene anaona ndikutulutsa anthu anga pakati pawo. 23 Komanso ndinalumbira kwa iwo mʼchipululu kuti ndidzawabalalitsira ku mitundu ina ya anthu ndiponso kuwamwaza mʼmayiko osiyanasiyana,+ 24 chifukwa sanatsatire zigamulo zanga, anakana malamulo anga,+ anadetsa sabata langa ndiponso ankalambira mafano onyansa a makolo awo.+ 25 Komanso ndinawasiya kuti azitsatira malamulo oipa ndi zigamulo zimene sizikanawathandiza kuti akhale ndi moyo.+ 26 Ndinawasiya kuti adziipitse ndi nsembe zawo pamene ankaponya pamoto mwana aliyense woyamba kubadwa.+ Ndinachita zimenezi kuti ndiwawononge nʼcholinga choti adziwe kuti ine ndine Yehova.”’
27 Choncho iwe mwana wa munthu, lankhula ndi Aisiraeli ndipo uwauze kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Makolo anu nawonso anandinyoza pondichitira zinthu mosakhulupirika. 28 Ine ndinawalowetsa mʼdziko limene ndinalumbira kuti ndidzawapatsa.+ Koma ataona mapiri onse ataliatali ndi mitengo ya masamba ambiri,+ anayamba kupereka nsembe zawo ndi zopereka zawo zimene sizinkandisangalatsa. Anapereka kafungo kosangalatsa* ka nsembe zawo ndiponso kuthira nsembe zawo zachakumwa pamalo amenewo. 29 Choncho ndinawafunsa kuti, ‘Kodi mumakachita chiyani kumalo okwezeka kumene mumapitako? (Malowo akudziwikabe kuti Malo Okwezeka mpaka lero.)’”’+
30 Tsopano uza nyumba ya Isiraeli kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Inu mukudziipitsa ngati mmene makolo anu anachitira potumikira mafano awo onyansa komanso kuwalambira.*+ 31 Ndipo mukupitiriza kudziipitsa mpaka lero popereka nsembe kwa mafano anu onse onyansa nʼkumawotcha ana anu pamoto.+ Ndiye kodi pa nthawi imodzimodziyo ndiyankhe zimene mukufunsa, inu a nyumba ya Isiraeli?”’+
‘Pali ine Mulungu wamoyo, sindiyankha zimene mukufunsazo,’+ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. 32 ‘Ndipo zimene mukuganiza zakuti: “Tiyeni tikhale ngati anthu a mitundu ina. Tikhale ngati mabanja amʼmayiko ena amene amalambira* mitengo ndi miyala,”+ sizichitika.’
33 ‘Pali ine Mulungu wamoyo,’ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, ‘Ine ndidzakulamulirani monga mfumu yanu. Ndidzakulamulirani ndi dzanja lamphamvu, mkono wotambasula ndi mkwiyo wosefukira.+ 34 Ndidzakuchotsani pakati pa mitundu ya anthu ndipo ndidzakusonkhanitsani pamodzi kuchokera kumayiko amene munabalalikirako. Ndidzakusonkhanitsani ndi dzanja lamphamvu, mkono wotambasula ndi mkwiyo wosefukira.+ 35 Ndidzakulowetsani mʼchipululu cha mitundu ya anthu ndipo kumeneko ndidzakuimbani mlandu pamasomʼpamaso.+
36 Ndidzakuimbani mlandu mofanana ndi mmene ndinaimbira mlandu makolo anu mʼchipululu chamʼdziko la Iguputo,’ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. 37 ‘Ndidzakudutsitsani pansi pa ndodo ya mʼbusa+ ndipo ndidzachititsa kuti musunge pangano. 38 Koma ndidzachotsa anthu opanduka komanso amene akundichimwira pakati panu.+ Chifukwa ndidzawatulutsa mʼdziko limene akukhalamo monga alendo, koma sadzalowa mʼdziko la Isiraeli,+ ndipo mudzadziwa kuti ine ndine Yehova.’
39 Inu a nyumba ya Isiraeli, Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: ‘Pitani, aliyense wa inu akatumikire mafano ake onyansa.+ Koma mudziwe kuti ngati simuyamba kundimvera, nthawi idzafika ndipo simudzathanso kudetsa dzina langa loyera popereka nsembe zanu ndiponso polambira mafano anu onyansa.’+
40 ‘Nyumba yonse ya Isiraeli idzanditumikira mʼphiri langa loyera,+ phiri lalitali lamʼdziko la Isiraeli,’+ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. ‘Kumeneko ndidzasangalala nanu ndipo ndidzafuna kuti mundibweretsere zopereka zanu komanso nsembe zanu zabwino kwambiri za zinthu zanu zonse zopatulika.+ 41 Chifukwa cha kafungo kosangalatsa,* ndidzasangalala nanu ndikadzakutulutsani pakati pa anthu a mitundu ina nʼkukusonkhanitsani pamodzi kuchokera mʼmayiko osiyanasiyana kumene munabalalikira.+ Komanso ndidzakusonyezani kuti ndine woyera ndipo anthu a mitundu ina adzaona zimenezi.+
42 Ndipo mudzadziwa kuti ine ndine Yehova,+ ndikadzakulowetsani mʼdziko la Isiraeli+ limene ndinalumbira kuti ndidzalipereka kwa makolo anu. 43 Kumeneko mudzakumbukira khalidwe lanu ndi zonse zomwe munkachita nʼkudziipitsa nazo+ ndipo mudzanyansidwa chifukwa cha zoipa zonse zimene munachita.+ 44 Kenako mudzadziwa kuti ine ndine Yehova ndikadzakuchitirani zimenezi chifukwa cha dzina langa+ osati mogwirizana ndi khalidwe lanu loipa kapena zinthu zoipa zimene munkachita, inu a nyumba ya Isiraeli,’ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”
45 Ndiyeno Yehova anandiuzanso kuti: 46 “Iwe mwana wa munthu, yangʼana mbali yakumʼmwera ndipo ulankhule zokhudza kumeneko. Ulosere zokhudza nkhalango ya dziko lakumʼmwera. 47 Uuze nkhalango yakumʼmwerayo kuti, ‘Imva mawu a Yehova. Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Ine ndikukuyatsa ndi moto.+ Motowo udzawotcha mtengo uliwonse wauwisi ndi mtengo uliwonse wouma umene uli mwa iwe. Malawi a motowo sadzazimitsidwa+ ndipo nkhope iliyonse, kuchokera kumʼmwera mpaka kumpoto idzapsa ndi moto. 48 Anthu onse adzaona kuti ine Yehova ndayatsa nkhalangoyo ndi moto ndipo sudzazimitsidwa.”’”+
49 Ine ndinanena kuti: “Mayo ine, Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa! Iwo akundinena kuti, ‘Kodi si miyambi imene akunenayi?’”
21 Yehova anandiuzanso kuti: 2 “Iwe mwana wa munthu, yangʼana ku Yerusalemu ndipo ulosere zimene zidzachitikire malo oyera komanso zimene zidzachitike mʼdziko la Isiraeli. 3 Uuze dziko la Isiraeli kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Ine ndidzakulanga ndipo ndidzasolola lupanga langa mʼchimake+ nʼkupha anthu ako olungama ndiponso anthu ako oipa. 4 Chifukwa chakuti ndidzapha anthu ako olungama ndi ochimwa, ndidzasolola lupanga langa mʼchimake nʼkupha anthu onse, kuchokera kumʼmwera mpaka kumpoto. 5 Anthu onse adzadziwa kuti ine Yehova ndasolola lupanga langa mʼchimake ndipo sindidzalibwezeramonso.”’+
6 Koma iwe mwana wa munthu, ubuule komanso kunjenjemera. Ubuule pamaso pawo mowawidwa mtima.+ 7 Ndiyeno akakufunsa kuti, ‘Nʼchifukwa chiyani ukubuula?’ Uwayankhe kuti, ‘Nʼchifukwa cha uthenga umene ndamva.’ Chifukwa zimene ndamvazo zidzachitikadi ndipo mtima wa munthu aliyense udzasungunuka ndi mantha. Manja a anthu onse adzafooka. Aliyense adzataya mtima ndipo mawondo onse azidzangochucha madzi.*+ ‘Uthengawo ufika ndithu ndipo zimene ukunena zidzachitikadi,’ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”
8 Yehova anandiuzanso kuti: 9 “Iwe mwana wa munthu, losera kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Nena kuti, ‘Lupanga! Lupanga+ lanoledwa ndi kupukutidwa. 10 Lanoledwa kuti liphe anthu ambiri. Lapukutidwa kuti liwale ngati mphezi.’”’”
“Kodi sitikuyenera kusangalala?”
“‘Kodi lupangalo lidzakana ndodo yachifumu ya mwana wanga,+ ngati mmene likukanira mtengo uliwonse?
11 Lupangalo ndalipereka kuti lipukutidwe komanso kuti ligwiritsidwe ntchito. Lupanga limeneli lanoledwa komanso kupukutidwa kuti liperekedwe mʼdzanja la munthu wakupha.+
12 Lira ndi kufuula+ iwe mwana wa munthu, chifukwa lupangalo labwera kuti lidzaphe anthu anga. Labwera kudzapha atsogoleri onse a Isiraeli.+ Atsogoleriwa adzaphedwa ndi lupanga pamodzi ndi anthu anga. Choncho menya pantchafu pako chifukwa cha chisoni. 13 Chifukwa anthu anga afufuzidwa,+ ndipo chidzachitike nʼchiyani ngati lupangalo litakana ndodo yachifumu? Ndodoyo sidzakhalaponso,’+ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.
14 Iwe mwana wa munthu, losera ndipo uwombe mʼmanja nʼkunena katatu mawu akuti, ‘Lupanga!’ Limeneli ndi lupanga lopha anthu, lupanga limene lapha anthu ambiri ndipo lawazungulira.+ 15 Mitima ya anthu idzasungunuka ndi mantha+ ndipo anthu ambiri adzagwa pamageti a mzinda wawo. Ndidzapha anthu ambiri ndi lupanga. Ndithu lupangalo likuwala ngati mphezi ndipo lapukutidwa kuti liphe anthu. 16 Iwe lupanga, uphe anthu mbali yakumanja ndi kumanzere. Pita kulikonse kumene akulozetsa. 17 Komanso ndidzawomba mʼmanja nʼkupereka chilango ndipo ndikadzatero mkwiyo wanga udzatha.+ Ineyo Yehova ndanena.”
18 Yehova anandiuzanso kuti: 19 “Koma iwe mwana wa munthu, jambula msewu umene ukuchokera mʼdzikolo. Pamalo ena msewuwo ugawikane nʼkukhala misewu iwiri. Mfumu ya Babulo imene ikubwera ndi lupanga idzasankha msewu umene ikuyenera kudutsa. Pamphambano pamene misewuyi yagawikana uikepo chikwangwani cholozera* kumene kuli mizindayo. 20 Usonyeze kuti msewu umodzi ndi woti mudzadutse lupanga likamadzapita kukawononga mzinda wa Raba+ wa mbadwa za Amoni, ndipo msewu winawo ndi woti lidzadutsemo likamadzapita ku Yuda kukawononga mzinda wa Yerusalemu umene uli ndi mpanda wolimba kwambiri.+ 21 Chifukwa mfumu ya Babulo idzaima pamalo pamene misewu iwiriyo yagawikana kuti iwombeze maula. Mfumuyo idzagwedeza mivi, idzafunsira kwa mafano ake* komanso idzawombeza maula pogwiritsa ntchito chiwindi cha nyama. 22 Maula amene adzakhale mʼdzanja lake lamanja, adzasonyeza kuti apite ku Yerusalemu, akaike zida zogumulira mzindawo, akalamule asilikali ake kuti aphe anthu, akalize chizindikiro cha nkhondo, akaike zida zogumulira mageti a mzindawo, akamange malo okwera omenyerapo nkhondo ndiponso kuti akamange mpanda womenyerapo nkhondo.+ 23 Kwa anthu* amene anachita nawo malumbiro, maulawo adzaoneka ngati abodza.+ Koma mfumuyo idzakumbukira zolakwa zawo ndipo idzawagwira.+
24 Choncho Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: ‘Mwachititsa kuti zolakwa zanu zikumbukiridwe. Mwachita zimenezi poonetsa poyera zolakwa zanuzo komanso pochititsa kuti machimo anu aoneke mʼzochita zanu zonse. Tsopano popeza mwakumbukiridwa, adzakutengani mokakamiza.’*
25 Koma iwe mtsogoleri wa Isiraeli, amene ndi woipa ndipo wavulazidwa koopsa,+ nthawi yoti ulandire chilango chomaliza yafika. 26 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: ‘Chotsa nduwira ndipo vula chisoti chachifumu.+ Zinthu zasintha tsopano.+ Kweza munthu wonyozeka+ ndipo tsitsa munthu wolemekezeka.+ 27 Ine ndidzawononga, ndidzawononga, ndidzawononga ufumu.* Ufumu umenewu sudzaperekedwa kwa wina aliyense mpaka atabwera amene ali woyenerera mwalamulo kuutenga,+ ndipo ndidzaupereka kwa iye.’+
28 Iwe mwana wa munthu, losera kuti, ‘Izi nʼzimene Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena zokhudza mbadwa za Amoni ndi mawu awo onyoza.’ Unene kuti, ‘Lupanga! Lupanga lasololedwa kuti liphe anthu. Lapukutidwa kuti liwononge komanso kuti liwale ngati mphezi. 29 Ngakhale kuti anakuuzani masomphenya abodza komanso analosera zabodza zokhudza inu, anthu anu adzaunjikidwa pamodzi ndi anthu amene adzaphedwe,* omwe ndi anthu oipa amene tsiku lawo loti alandire chilango chomaliza lafika. 30 Bwezerani lupanga mʼchimake. Ndidzakuweruzirani kumalo amene munabadwira,* mʼdziko limene munachokera. 31 Ndidzakukhuthulirani mkwiyo wanga. Ndidzakupemererani ndi moto wa ukali wanga, ndipo ndidzakuperekani mʼmanja mwa anthu ankhanza, akatswiri odziwa kuwononga.+ 32 Mudzakhala ngati nkhuni pamoto.+ Magazi anu adzakhetsedwa mʼdzikolo ndipo simudzakumbukiridwanso, chifukwa ine Yehova ndanena.’”
22 Yehova analankhulanso nane kuti: 2 “Iwe mwana wa munthu, kodi ndiwe wokonzeka kupereka uthenga wachiweruzo kwa mzinda* umene uli ndi mlandu wa magaziwu+ komanso kuudziwitsa zonyansa zake zonse?+ 3 Unene kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Iwe mzinda umene uli ndi mlandu wokhetsa magazi,+ umene nthawi yako yoti uweruzidwe ikubwera,+ umenenso umapanga mafano onyansa* kuti udzidetse nawo,+ 4 magazi amene wakhetsa apangitsa kuti ukhale ndi mlandu+ ndipo mafano ako onyansa apangitsa kuti ukhale wodetsedwa.+ Wafupikitsa masiku a moyo wako ndipo ulangidwa posachedwapa. Nʼchifukwa chake ndachititsa kuti anthu a mitundu ina azikunyoza komanso kuti anthu amʼmayiko onse azikuseka.+ 5 Mayiko amene uli nawo pafupi ndiponso amene ali kutali ndi iwe adzakuseka,+ iwe amene dzina lako ndi lodetsedwa komanso uli ndi mavuto ambiri. 6 Taona! Mtsogoleri aliyense wa Isiraeli pakati pako akugwiritsa ntchito udindo wake kuti akhetse magazi.+ 7 Mwa iwe muli anthu amene amanyoza bambo awo komanso mayi awo.+ Mlendo amamuchitira zinthu mwachinyengo ndipo amazunza mwana wamasiye ndi mkazi wamasiye.”’”+
8 “‘Iwe wanyoza malo anga oyera ndipo wadetsa sabata langa.+ 9 Mwa iwe muli anthu amiseche amene amafuna kukhetsa magazi.+ Mulinso anthu amene amadya chakudya choperekedwa nsembe kwa mafano mʼmapiri ndipo amachita khalidwe lonyansa pakati panu.+ 10 Mwa iwe muli anthu amene salemekeza pogona pa bambo awo*+ ndipo amakakamiza mkazi wodetsedwa amene akusamba kuti agone naye.+ 11 Mwa iwe muli munthu amene amachita zonyansa ndi mkazi wa mnzake.+ Wina amadetsa mpongozi wake wamkazi pochita naye khalidwe lonyansa+ ndipo wina amagona ndi mchemwali wake, mwana wamkazi wa bambo ake enieni.+ 12 Mwa iwe muli anthu amene akulandira ziphuphu kuti akhetse magazi.+ Iwe ukabwereketsa ndalama umafuna kuti akupatse chiwongoladzanja+ kapena kuti upeze phindu* ndipo ukubera anzako ndalama mwachinyengo.+ Ndithu, ine wandiiwaliratu,’ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.
13 ‘Ine ndawomba mʼmanja chifukwa chonyansidwa ndi phindu lachinyengo limene wapeza komanso chifukwa cha magazi amene anakhetsedwa pakati pako. 14 Kodi udzapitiriza kukhala wolimba mtima ndipo kodi dzanja lako lidzakhalabe lamphamvu pa tsiku limene ndidzakulange?+ Ine Yehova ndanena ndipo ndidzachitapo kanthu. 15 Anthu ako ndidzawabalalitsira ku mitundu ina ya anthu ndipo ndidzawamwaza mʼmayiko osiyanasiyana.+ Komanso ndidzathetsa khalidwe lako lonyansa.+ 16 Udzanyozeka pamaso pa mitundu ina ya anthu ndipo udzadziwa kuti ine ndine Yehova.’”+
17 Yehova anandiuzanso kuti: 18 “Iwe mwana wa munthu, kwa ine nyumba ya Isiraeli yakhala ngati zinthu zachabechabe zotsalira poyenga zitsulo. Onse ali ngati kopa,* tini, chitsulo ndi mtovu zimene zili mungʼanjo. Iwo akhala ngati zinthu zimene zimatsalira akayenga siliva.+
19 Choncho Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: ‘Chifukwa chakuti nonsenu mwakhala ngati zinthu zachabechabe zotsalira poyenga zitsulo,+ ine ndikusonkhanitsani pamodzi mu Yerusalemu. 20 Ndidzakusonkhanitsani pamodzi ngati mmene amasonkhanitsira siliva, kopa, chitsulo, mtovu ndi tini mungʼanjo kuti azikolezere moto nʼkuzisungunula. Ndidzachita zimenezi nditakwiya komanso mwaukali ndipo ndidzakukolezerani moto nʼkukusungunulani.+ 21 Ndidzakusonkhanitsani pamodzi nʼkukukolezerani moto wa mkwiyo wanga,+ ndipo mudzasungunuka mumzindawo.+ 22 Mofanana ndi siliva amene amamusungunulira mungʼanjo, inenso ndidzakusungunulirani mumzindawo. Choncho mudzadziwa kuti ine Yehova ndadzakukhuthulirani mkwiyo wanga.’”
23 Yehova anandiuzanso kuti: 24 “Iwe mwana wa munthu, uza dzikoli kuti, ‘Iwe ndi dziko limene silidzayeretsedwa ndipo mwa iwe simudzagwa mvula pa tsiku limene ndidzakusonyeze mkwiyo wanga. 25 Aneneri ako akukonza chiwembu mʼdzikoli.+ Iwo ali ngati mkango wobangula umene wagwira nyama+ ndipo akupha anthu. Akulanda anthu chuma ndi zinthu zawo zamtengo wapatali. Apangitsa kuti akazi amasiye achuluke mʼdzikolo. 26 Ansembe ako aphwanya chilamulo changa+ ndipo akupitiriza kuipitsa malo anga oyera.+ Sakusiyanitsa zinthu zoyera ndi zinthu wamba+ ndipo akulephera kuuza anthu kuti zinthu zodetsedwa ndi ziti komanso zinthu zoyera ndi ziti.+ Iwo akukana kusunga sabata langa ndipo adetsa dzina langa pakati pawo. 27 Akalonga amʼdzikoli ali ngati mimbulu yomwe ikukhadzula nyama. Iwo akukhetsa magazi ndiponso kupha anthu nʼcholinga chopeza phindu mwachinyengo.+ 28 Koma aneneri amʼdzikomo apaka laimu zochita za akalongawo. Iwo amaona masomphenya onama ndipo amalosera zinthu zabodza.+ Aneneriwo amanena kuti: “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti,” pamene Yehova sananene chilichonse. 29 Anthu amʼdzikolo abera anthu mwachinyengo komanso achita zauchifwamba.+ Iwo achitira nkhanza anthu ovutika ndi osauka. Abera mlendo mwachinyengo komanso sanamuchitire zinthu mwachilungamo.’
30 ‘Ndinafunafuna munthu pakati pawo amene angathe kukonzanso mpanda wamiyala kapena kuima pamalo ogumuka a mpandawo kuti ateteze dzikolo nʼcholinga choti ine ndisaliwononge,+ koma sindinapeze aliyense. 31 Choncho ndidzawakhuthulira mkwiyo wanga ndipo ndidzawawononga onse ndi moto wa ukali wanga. Ndidzawalanga mogwirizana ndi zochita zawo,’ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”
23 Yehova anandiuzanso kuti: 2 “Iwe mwana wa munthu, panali akazi awiri amene anali ana a mayi mmodzi.+ 3 Akazi amenewa anayamba kuchita uhule mʼdziko la Iguputo.+ Anayamba uhulewu ali atsikana angʼonoangʼono. Kumeneko amuna anafinya mabere awo komanso kusisita pamtima pawo ali anamwali. 4 Wamkulu dzina lake anali Ohola,* wamngʼono anali Oholiba.* Akazi amenewa anakhala anga ndipo anabereka ana aamuna ndi aakazi. Ohola akuimira Samariya+ ndipo Oholiba akuimira Yerusalemu.
5 Ohola anayamba kuchita uhule+ ngakhale kuti anali mkazi wanga. Ankalakalaka kugona ndi amuna amene ankamukonda kwambiri+ omwe ndi Asuri amene ankakhala moyandikana naye.+ 6 Amunawo anali abwanamkubwa amene ankavala zovala zabuluu ndiponso achiwiri kwa olamulira. Onsewa anali anyamata osiririka, akatswiri okwera mahatchi. 7 Iye anapitiriza kuchita uhule ndi amuna onse olemekezeka amʼdziko la Asuri ndipo anadziipitsa+ ndi mafano onyansa* a amuna amene ankawalakalakawo. 8 Iye sanasiye uhule umene ankachita ali ku Iguputo. Aiguputowo ankagona naye kuyambira ali kamtsikana. Iwo ankasisita pamtima pake ali namwali ndipo ankachita naye zachiwerewere.+ 9 Choncho ndinamʼpereka mʼmanja mwa anthu amene ankamukonda kwambiri, omwe ndi amuna amʼdziko la Asuri+ amene ankalakalaka kugona naye. 10 Amunawo anamuvula,+ anagwira ana ake aamuna ndi aakazi+ ndipo iyeyo anamupha ndi lupanga. Iye anatchuka ndi khalidwe loipa pakati pa akazi ena ndipo anapatsidwa chilango.
11 Mchemwali wake Oholiba ataona zimenezi, chilakolako chake chinafika poipa kwambiri ndipo uhule wake unafika poipa kuposa wa mkulu wake.+ 12 Iye ankalakalaka kwambiri kugona ndi amuna amʼdziko la Asuri+ omwe anayandikana nawo. Amuna amenewa anali abwanamkubwa ndi achiwiri kwa olamulira amene ankavala zovala zokongola ndipo anali akatswiri okwera mahatchi. Onsewa anali anyamata osiririka. 13 Oholiba atadziipitsa, ine ndinaona kuti akazi awiri onsewa anali ndi khalidwe lofanana.+ 14 Koma iye anapitiriza kuwonjezera zochita zake zauhule. Iye anaona zithunzi za amuna zogoba pakhoma, zithunzi zogoba za Akasidi zopaka penti yofiira. 15 Anaona zithunzi za amuna atavala malamba mʼchiuno ndipo kumutu kwawo anavala nduwira zazitali zolendewera. Amuna onsewo ankaoneka ngati asilikali komanso ngati amuna a ku Babulo, obadwira mʼdziko la Akasidi. 16 Ataona zithunzizo, anayamba kulakalaka kwambiri kugona ndi amunawo ndipo anatumiza anthu ku Kasidi+ kuti akawaitane. 17 Choncho amuna a ku Babulowo ankabwera pabedi pake nʼkumachita zachikondi ndipo anamuipitsa ndi chiwerewere chawo. Amunawo atamuipitsa, iye anawasiya chifukwa anayamba kunyansidwa nawo.
18 Oholiba atapitiriza kuchita uhule mopanda manyazi komanso kudzivula,+ ine ndinamusiya chifukwa chonyansidwa naye, ngati mmene ndinasiyira mchemwali wake chifukwa chonyansidwa naye.+ 19 Oholiba anapitiriza kuwonjezera zochita zake zauhule+ mpaka kufika pokumbukira masiku amene anali kamtsikana, pamene ankachita uhule mʼdziko la Iguputo.+ 20 Iye ankalakalaka kugona ndi anthu amene ankawakonda mofanana ndi adzakazi* amene amuna awo ali ndi ziwalo ngati za abulu amphongo komanso ngati ziwalo za mahatchi amphongo. 21 Iwe unkalakalaka khalidwe lonyansa limene unkachita ku Iguputo+ uli kamtsikana pamene amuna ankasisita mabere ako.+
22 Choncho iwe Oholiba, Yehova Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: ‘Ndichititsa kuti amuna omwe unkawakonda,+ amene unawasiya chifukwa chonyansidwa nawo akuukire. Ndidzawabweretsa kuchokera kumbali zonse kuti adzakuukire.+ 23 Ndidzabweretsa amuna a ku Babulo,+ Akasidi onse,+ amuna a ku Pekodi,+ a ku Sowa, a ku Kowa pamodzi ndi amuna onse amʼdziko la Asuri. Onsewa ndi anyamata osiririka, abwanamkubwa, achiwiri kwa olamulira, asilikali komanso amuna osankhidwa mwapadera.* Onsewa ndi akatswiri okwera mahatchi. 24 Iwo adzabwera kudzakuukira ndipo akamadzabwera, padzamveka phokoso la magaleta ankhondo ndi la mawilo. Adzabwera ndi gulu lalikulu la asilikali, atatenga zishango zazikulu, zishango zazingʼono ndiponso atavala zipewa. Iwo adzakuzungulira ndipo ndidzawapatsa mphamvu zoweruza, moti adzakuweruza mmene akufunira.+ 25 Ndidzasonyeza mkwiyo wanga pa iwe ndipo iwo adzakulanga mwaukali. Adzakudula mphuno ndi makutu ndipo ena a inu amene adzatsale adzaphedwa ndi lupanga. Iwo adzatenga ana ako aamuna ndi aakazi ndipo anthu ena amene adzatsale adzawotchedwa ndi moto.+ 26 Adzakuvula zovala zako+ ndipo adzatenga zinthu zako zodzikongoletsera.+ 27 Ine ndidzathetsa khalidwe lako lonyansa ndiponso uhule wako+ umene unauyambira mʼdziko la Iguputo.+ Udzasiya kuyangʼana amuna a ku Iguputo ndipo dziko la Iguputo sudzalikumbukiranso.’
28 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: ‘Ndatsala pangʼono kukupereka mʼmanja mwa amuna amene ukudana nawo, amuna amene unawasiya chifukwa chonyansidwa nawo.+ 29 Iwo adzakuchitira zinthu zosonyeza kuti amadana nawe ndipo adzatenga zinthu zonse zimene unazipeza movutikira+ nʼkukusiya wosavala ndi wamaliseche. Umaliseche umene unauonetsa pochita chiwerewere, khalidwe lako lonyansa ndiponso uhule wako zidzaonekera poyera.+ 30 Adzakuchitira zimenezi chifukwa chakuti unkalakalaka anthu a mitundu ina ngati hule+ komanso chifukwa chakuti unadziipitsa ndi mafano awo onyansa.+ 31 Iwe wachita zinthu zofanana ndi zimene mchemwali wako anachita+ ndipo ndidzakupatsa kapu yake.’+
32 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti:
‘Udzamwa zamʼkapu ya mkulu wako, yomwe ndi yaitali komanso yaikulu.+
Ndipo anthu azidzakuseka komanso kukunyoza chifukwa mʼkapumo muli zambiri.+
33 Udzaledzera kwambiri ndipo udzakhala ndi chisoni.
Udzaledzera ndi zinthu zamʼkapu ya mchemwali wako Samariya,
Zinthu zochititsa mantha kwambiri komanso zowononga.
34 Iwe udzamwa ndi kugugudiza zamʼkapuyo+ ndipo udzatafuna zidutswa za kapuyo
Kenako udzakhadzula mabere ako.
“Ine ndanena,” akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.’
35 Choncho Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: ‘Chifukwa chakuti wandiiwala ndipo sukundilabadiranso,*+ udzalangidwa chifukwa cha khalidwe lako lonyansa ndi zochita zako zauhule.’”
36 Kenako Yehova anandiuza kuti: “Iwe mwana wa munthu, kodi ndiwe wokonzeka kupereka uthenga wachiweruzo kwa Ohola ndi Oholiba+ komanso kuwauza zinthu zonyansa zimene achita? 37 Iwo achita chigololo*+ ndipo mʼmanja mwawo muli magazi. Kuwonjezera pa kuchita chigololo ndi mafano awo onyansa, iwo awotcha pamoto ana awo aamuna amene anandiberekera kuti akhale chakudya cha mafano awowo.+ 38 Komanso anandichitira zinthu izi: Pa tsikulo anaipitsa malo anga opatulika ndiponso sabata langa. 39 Atapha ana awo aamuna nʼkuwapereka nsembe kwa mafano onyansa,+ tsiku lomwelo anabwera kumalo anga opatulika kudzawadetsa.+ Izi ndi zimene anachita mʼnyumba yanga. 40 Kuwonjezera apo, akaziwo anatumiza uthenga kwa amuna ochokera kutali kuti abwere.+ Amunawo akubwera, iwe unasamba nʼkupaka zodzikongoletsera mʼmaso mwako ndipo unavala zodzikongoletsera.+ 41 Kenako unakhala pampando wabwino kwambiri+ ndipo patsogolo pake panali tebulo loyalidwa bwino.+ Patebulopo unaikapo zofukiza zanga zonunkhira+ komanso mafuta anga.+ 42 Kumeneko kunamveka phokoso la gulu la anthu amene akucheza mosangalala. Pagulu limeneli panalinso zidakwa zimene anazibweretsa kuchokera kuchipululu. Amuna amenewa anaveka akaziwo zibangili ndi zipewa zachifumu zokongola kumutu kwawo.
43 Kenako ndinalankhula zokhudza mkazi amene anali atatoperatu chifukwa cha chigololo kuti: ‘Komabe apitiriza kuchita uhule.’ 44 Choncho amuna aja anapitiriza kupita kwa iye ngati mmene amuna amapitira kwa hule. Umu ndi mmene ankapitira kwa Ohola ndi Oholiba, akazi akhalidwe lonyansa. 45 Koma amuna olungama adzamupatsa chiweruzo choyenera chimene amapereka kwa munthu wachigololo+ komanso wokhetsa magazi.+ Chifukwa iwowa ndi akazi achigololo ndipo mʼmanja mwawo muli magazi.+
46 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: ‘Adzawabweretsera gulu la asilikali kuti lidzawaukire nʼkuwasandutsa chinthu chochititsa mantha komanso chinthu choyenera kutengedwa ndi adani.+ 47 Asilikaliwo adzawagenda ndi miyala+ nʼkuwapha ndi malupanga. Adzaphanso ana awo aamuna ndi aakazi+ ndipo adzawotcha nyumba zawo.+ 48 Ndidzathetsa khalidwe lonyansa mʼdzikoli ndipo akazi onse adzaphunzirapo kanthu, moti sadzatengera khalidwe lanu lonyansa.+ 49 Asilikaliwo adzakulangani chifukwa cha khalidwe lanu lonyansa komanso machimo amene munachita ndi mafano anu onyansa, ndipo mudzadziwa kuti ine ndine Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.’”+
24 Yehova analankhulanso nane mʼchaka cha 9, mʼmwezi wa 10, pa tsiku la 10 la mweziwo, kuti: 2 “Iwe mwana wa munthu, lemba deti lalero,* ulembe tsiku lalero. Lero mfumu ya Babulo yayamba kuukira mzinda wa Yerusalemu.+ 3 Nena mwambi wokhudza anthu opanduka. Unene zokhudza anthu amenewa kuti:
‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti:
“Ika mphika* pamoto ndipo uthiremo madzi.+
4 Uikemo nthuli za nyama,+ nthuli zabwinozabwino.
Uikemo mwendo wamʼmbuyo ndi wakutsogolo. Udzazemo mafupa abwino kwambiri.
5 Tenga nkhosa yabwino kwambiri+ ndipo usonkhezere nkhuni kuzungulira mphikawo.
Uwiritse nthuli za nyamazo limodzi ndi mafupa amene ali mumphikawo.”’
6 Choncho Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti:
‘Tsoka mzinda wokhetsa magazi,+ umene uli ngati mphika wadzimbiri, womwe dzimbiri lakelo silikuchoka.
Muchotsemo nthulizo imodziimodzi.+ Musachite maere pa nthulizo.
7 Chifukwa magazi amene mzindawo wakhetsa ali mkati mwake.+ Wathira magaziwo pathanthwe lopanda chilichonse.
Mzindawo sunathire magaziwo pansi kuti uwakwirire ndi dothi.+
8 Ine ndathira magazi amene mzindawo wakhetsa pathanthwe lopanda chilichonse
Kuti asakwiriridwe.+
Ndachita zimenezi kuti mkwiyo wanga uyakire mzindawo nʼkuulanga chifukwa cha zochita zake.’
9 Choncho Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti:
‘Tsoka mzinda wokhetsa magazi!+
Ine ndidzaunjika mulu waukulu wa nkhuni.
10 Sonkhanitsani zikuni zambiri nʼkukoleza moto,
Wiritsani nyamayo mpaka ipse. Khuthulani msuzi wake ndipo mafupawo muwasiye kuti apserere.
11 Ikani mphika wakopa* wopanda kanthu pamakala amoto kuti utenthe kwambiri
Ndipo ufiire chifukwa cha kutentha.
Zonyansa zake zisungunukemo+ ndipo dzimbiri lake lipse ndi motowo.
12 Ntchito yake ndi yaikulu komanso yotopetsa,
Chifukwa dzimbiri lake, lomwe ndi lambiri, silikuchoka.+
Uponyeni pamoto ndi dzimbiri lakelo.’
13 ‘Ndiwe wodetsedwa chifukwa cha khalidwe lako lonyansa.+ Ine ndinayesa kukuyeretsa, koma sunayere chifukwa zonyansa zako sizinachoke. Sudzayera mpaka mkwiyo wanga utatha.+ 14 Ine Yehova ndanena ndipo zidzachitikadi. Ndidzachitapo kanthu mosazengereza, popanda kumva chisoni kapena kusintha maganizo.+ Iwo adzakuweruza mogwirizana ndi njira zako komanso zochita zako,’ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”
15 Yehova analankhulanso nane kuti: 16 “Iwe mwana wa munthu, ine ndichititsa kuti mkazi wako afe mwadzidzidzi.+ Koma iwe usamve chisoni,* kulira kapena kugwetsa misozi. 17 Ulire mosatulutsa mawu ndipo usachite miyambo yamaliro.+ Uvale nduwira kumutu+ ndipo uvale nsapato zako.+ Usaphimbe ndevu zako zapamlomo+ ndipo usadye chakudya chimene anthu angakupatse.”+
18 Mʼmawa ndinalankhula ndi anthu ndipo madzulo, mkazi wanga anamwalira. Choncho mʼmawa wa tsiku lotsatira ndinachita zonse zimene anandilamula. 19 Anthu ankandifunsa kuti: “Kodi sutiuza kuti zimene ukuchitazi zikutikhudza bwanji?” 20 Ine ndinawayankha kuti: “Yehova wandiuza kuti, 21 ‘Uza nyumba ya Isiraeli kuti: “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Ndatsala pangʼono kudetsa malo anga opatulika,+ chinthu chimene mumachinyadira kwambiri, chinthu chimene mumachikonda komanso chapamtima panu. Ana anu aamuna ndi aakazi amene munawasiya mumzindawo adzaphedwa ndi lupanga.+ 22 Zikadzatero inu mudzachita zimene ine ndachita. Simudzaphimba ndevu zanu zapamlomo ndipo simudzadya chakudya chimene anthu adzakupatseni.+ 23 Mudzavala nduwira zanu ndiponso nsapato zanu. Simudzamva chisoni kapena kulira pagulu. Mʼmalomwake, mudzavutika chifukwa cha zolakwa zanu+ ndipo mudzalira mosatulutsa mawu. 24 Ezekieli wakhala chizindikiro kwa inu.+ Mudzachita zonse zimene iye wachita. Tsokali likadzakugwerani, mudzadziwa kuti ine ndine Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.’”’”
25 “Koma iwe mwana wa munthu, pa tsiku limene ndidzawachotsere mpanda wawo wolimba, chinthu chokongola chimene chimawasangalatsa, chinthu chimene amachikonda komanso chapamtima pawo, limodzi ndi ana awo aamuna ndi aakazi,+ 26 munthu amene wapulumuka adzabwera kwa iwe nʼkudzakuuza zimene zachitika.+ 27 Pa tsiku limenelo udzatsegula pakamwa pako nʼkulankhula ndi munthu amene wapulumukayo ndipo sudzakhalanso chete.+ Iwe udzakhala chizindikiro kwa iwo, ndipo adzadziwa kuti ine ndine Yehova.”
25 Yehova anandiuzanso kuti: 2 “Iwe mwana wa munthu, yangʼana kwa Aamoni+ ndipo ulosere zoipa zimene zidzawachitikire.+ 3 Uuze Aamoniwo kuti, ‘Imvani mawu a Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Inu munanena kuti ‘Eyaa! Zakhala bwino.’ Munanena zimenezi malo anga opatulika atadetsedwa, dziko la Isiraeli litasanduka bwinja komanso nyumba ya Yuda itatengedwa kupita ku ukapolo. 4 Pa chifukwa chimenechi, ndikuperekani kwa anthu a Kumʼmawa kuti mukhale chuma chawo. Iwo adzamanga misasa yokhala ndi mipanda komanso adzakhoma matenti awo mʼdziko lanu. Adzadya zokolola zanu ndipo adzamwa mkaka wa ziweto zanu. 5 Mzinda wa Raba+ ndidzausandutsa malo odyetserako ngamila, ndipo dziko la Aamoni ndidzalisandutsa malo opumilako ziweto ndipo mudzadziwa kuti ine ndine Yehova.”’”
6 “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: ‘Chifukwa chakuti munawomba mʼmanja+ ndi kuponda pansi mwamphamvu, komanso munasangalala monyoza poona zimene zinachitikira dziko la Isiraeli,+ 7 ine nditambasula dzanja langa nʼkukulangani ndipo ndikuperekani kwa anthu a mitundu ina kuti akutengeni. Ndidzakuwonongani kuti musakhalenso mtundu wa anthu ndipo ndidzakuchotsani pakati pa mayiko ena.+ Ndidzakufafanizani ndipo mudzadziwa kuti ine ndine Yehova.’
8 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: ‘Chifukwa chakuti Mowabu+ ndi Seiri+ anena kuti, “Taonani! Nyumba ya Yuda ili ngati mitundu ina yonse ya anthu,” 9 ine ndidzachititsa kuti adani aukire mizinda imene ili mʼmalire mwa Mowabu,* kuphatikizapo mizinda yake yabwino kwambiri.* Mizindayo ndi Beti-yesimoti, Baala-meoni mpaka kukafika ku Kiriyataimu.+ 10 Ndidzapereka Mowabu limodzi ndi Aamoni kwa anthu a Kumʼmawa+ kuti akhale chuma chawo. Ndidzachita zimenezi kuti Aamoni asadzakumbukiridwenso pakati pa mitundu ya anthu.+ 11 Ndidzapereka chiweruzo mʼdziko la Mowabu+ ndipo adzadziwa kuti ine ndine Yehova.’
12 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: ‘Edomu wabwezera zoipa kwa nyumba ya Yuda ndipo wapalamula mlandu waukulu chifukwa chowabwezera.+ 13 Choncho Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Nditambasulanso dzanja langa nʼkulanga Edomu ndipo ndipha anthu ndi ziweto mʼdzikolo, moti ndidzalisandutsa bwinja.+ Anthu adzaphedwa ndi lupanga kuyambira ku Temani mpaka ku Dedani.+ 14 ‘Ine ndidzabwezera Edomu pogwiritsa ntchito anthu anga Aisiraeli.+ Aisiraeliwo adzachitira Edomu mogwirizana ndi mkwiyo komanso ukali wanga, ndipo iwo adzadziwa kuti ine ndikuwabwezera,’+ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”’
15 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: ‘Popeza Afilisiti akupitiriza kuchitira zoipa Aisiraeli chifukwa chodana nawo, iwo akufuna kubwezera komanso kuwononga Aisiraeliwo mwankhanza.*+ 16 Choncho Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Ine ndikutambasula dzanja langa kuti ndilange Afilisiti,+ ndipo ndidzapha Akereti+ nʼkuwononga anthu onse omwe anatsala, amene amakhala mʼmbali mwa nyanja.+ 17 Anthu amenewa ndidzawachitira zinthu zopweteka powabwezera ndipo ndidzawalanga mwaukali. Ndikadzawalanga, adzadziwa kuti ine ndine Yehova.”’”
26 Mʼchaka cha 11, pa tsiku loyamba la mwezi, Yehova analankhula nane kuti: 2 “Iwe mwana wa munthu, Turo wanena Yerusalemu+ kuti, ‘Eyaa! Zakhala bwino. Mzinda umene unkakopa anthu a mitundu ina wathyoledwa.+ Tsopano zinthu zindiyendera bwino ndipo ndilemera chifukwa mzindawo wawonongedwa.’ 3 Choncho Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Ine ndikuukira iwe Turo ndipo ndikutumizira mayiko ambiri kuti adzamenyane nawe. Iwo adzabwera ngati mafunde amʼnyanja. 4 Mayikowo adzagwetsa mipanda ya Turo komanso kugumula nsanja zake.+ Ine ndidzapala dothi lake nʼkumusandutsa thanthwe losalala lopanda kanthu. 5 Iye adzakhala malo oyanikapo makoka pakati pa nyanja.’+
‘Ine ndanena ndipo anthu a mitundu ina adzalanda zinthu zake,’ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. 6 ‘Anthu amʼmidzi yake imene ili* kunja kwa mzindawo adzaphedwa ndi lupanga ndipo anthu adzadziwa kuti ine ndine Yehova.’
7 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Ine ndikutumiza Nebukadinezara* mfumu ya Babulo, mfumu ya mafumu,+ kuchokera kumpoto+ kuti akaukire Turo. Iye adzapita ndi mahatchi,+ magaleta ankhondo,+ asilikali apamahatchi ndi gulu la asilikali ambiri. 8 Anthu omwe akukhala mʼmidzi yako imene ili kunja kwa mzindawu adzawapha ndi lupanga. Iye adzamanga mpanda womenyerapo nkhondo komanso malo okwera omenyerapo nkhondo kuti amenyane nawe ndipo adzakuukira ndi chishango chachikulu. 9 Mfumuyo idzagumula mpanda wako ndi chida chogumulira,* ndipo idzagwetsa nsanja zako pogwiritsa ntchito nkhwangwa zake.* 10 Mahatchi ake adzakhala ambiri moti adzakukwirira ndi fumbi. Phokoso la asilikali apamahatchi, mawilo ake ndi magaleta zidzachititsa kuti mpanda wako unjenjemere akamadzalowa pamageti ako ngati anthu amene akulowa mumzinda umene mpanda wake ndi wogumuka kuti augonjetse. 11 Ziboda za mahatchi ake zidzapondaponda mʼmisewu yako yonse.+ Iye adzapha anthu ako ndi lupanga ndipo zipilala zako zikuluzikulu zidzagwa. 12 Iwo adzakulanda chuma chako ndi malonda ako.+ Adzagwetsa mpanda wako ndi nyumba zako zabwino kwambiri. Kenako miyala yako, zinthu zako zamatabwa komanso dothi lako adzaziponya mʼmadzi.’
13 ‘Ndidzathetsa phokoso la nyimbo zako ndipo phokoso la azeze ako silidzamvekanso.+ 14 Ndidzakusandutsa thanthwe losalala lopanda kanthu ndipo udzakhala malo oyanikapo makoka.+ Mzinda wako sudzamangidwanso chifukwa ine Yehova ndanena,’ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.
15 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wauza mzinda wa Turo kuti: ‘Kodi zilumba sizidzagwedezeka chifukwa cha phokoso la kugwa kwako, kubuula kwa anthu amene avulazidwa koopsa* komanso chifukwa cha kuphedwa kwa anthu ako ambiri?+ 16 Akalonga* onse akunyanja adzatsika mʼmipando yawo yachifumu nʼkuvula mikanjo yawo* komanso zovala zawo za nsalu yopeta. Iwo azidzanjenjemera chifukwa cha mantha. Adzakhala padothi ndipo nthawi zonse azidzanjenjemera nʼkumakuyangʼanitsitsa modabwa.+ 17 Iwo adzakuimbira nyimbo yoimba polira.+ Azidzati:
“Iwe mzinda wotamandika, zoona wawonongekadi!+ Mwa iwe munkakhala anthu ochokera kunyanja.
Iwe ndi anthu ako munali amphamvu panyanja,+
Munkachititsa mantha anthu onse okhala padziko lapansi.
18 Pa tsiku limene udzagwe, zilumba zidzanjenjemera,
Zilumba zamʼnyanja zidzasokonezeka iweyo ukadzawonongedwa.”’+
19 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: ‘Ndikadzakuwononga ngati mizinda imene simukukhala anthu, ndikadzakubweretsera madzi ambiri, ndipo madzi amphamvu akadzakumiza,+ 20 ndidzakutsitsira mʼdzenje* limodzi ndi anthu enanso amene akutsikira mʼmanda momwe muli anthu amene anafa kalekale. Ndidzakuchititsa kuti ukhale mʼmalo otsika kwambiri mofanana ndi malo ena akalekale amene anawonongedwa. Udzakhala kumeneko pamodzi ndi ena onse amene akutsikira kumanda+ kuti anthu asadzakhalenso mwa iwe. Kenako ndidzalemekeza* dziko la anthu amoyo.
21 Ndidzakugwetsera zoopsa modzidzimutsa ndipo sudzakhalaponso.+ Anthu adzakufunafuna koma sudzapezeka mpaka kalekale,’ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”
27 Yehova analankhulanso nane kuti: 2 “Iwe mwana wa munthu, imba nyimbo yoimba polira yokhudza Turo.+ 3 Uimbire Turo kuti,
‘Iwe amene ukukhala polowera mʼnyanja,
Iwe amene ukuchita malonda ndi anthu amʼzilumba zambiri,
Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti:
“Iwe Turo wanena kuti, ‘Ine ndine wokongola kwambiri.’+
4 Madera ako ali mkatikati mwa nyanja,
Ndipo amisiri amene anakumanga anakukongoletsa kwambiri.
5 Anakupanga ndi matabwa a mtengo wa junipa* ochokera ku Seniri,+
Ndipo anatenga mkungudza wa ku Lebanoni kuti ukhale mtengo wako womangirirapo chinsalu choyendetsera ngalawa.
6 Zopalasira zako anazipanga ndi mitengo ikuluikulu ya ku Basana,
Ndipo mbali yakutsogolo kwako anaipanga ndi matabwa a paini, nʼkuikongoletsa ndi minyanga yochokera kuzilumba za Kitimu.+
7 Chinsalu chako choyendetsera ngalawa anachipanga ndi nsalu za mitundu yosiyanasiyana zochokera ku Iguputo,
Ndipo pamwamba pako anaphimbapo ndi chinsalu chopangidwa ndi ulusi wabuluu komanso ubweya wa nkhosa wapepo wochokera kuzilumba za Elisha.+
8 Anthu a ku Sidoni ndi ku Arivadi+ ndi amene ankakupalasa.
Iwe Turo, akatswiri ako odziwa kuyendetsa sitima zapamadzi ndi amene ankakuyendetsa.+
9 Amuna odziwa ntchito* komanso aluso a ku Gebala+ ndi amene ankamata molumikizira matabwa ako.+
Sitima zonse zapanyanja ndi anthu amene ankaziyendetsa ankabwera kwa iwe kudzagulitsa malonda.
10 Amuna a ku Perisiya, ku Ludi ndi ku Puti+ anali mʼgulu lako lankhondo, anali mʼgulu la asilikali ako.
Iwo ankapachika zishango ndi zipewa zawo pamakoma ako ndipo anakubweretsera ulemerero.
11 Amuna a ku Arivadi amene ali mʼgulu la asilikali ako anaima pamwamba pa mpanda wako kuzungulira mzinda wonse,
Ndipo amuna olimba mtima ankalondera nsanja zako.
Iwo anapachika zishango zawo zozungulira mʼmakoma kuzungulira mpanda wako wonse,
Ndipo anachititsa kuti ukhale wokongola kwambiri.
12 Tarisi+ ankachita nawe malonda chifukwa unali ndi chuma chochuluka.+ Anakupatsa siliva, chitsulo, tini ndi mtovu kuti atenge katundu wako.+ 13 Iwe unkachita malonda ndi Yavani, Tubala+ ndi Meseki.+ Iwo ankakupatsa akapolo+ ndi zinthu zakopa kuti iwe uwapatse katundu wako. 14 Ana a Togarima+ anapereka mahatchi ndi nyulu posinthanitsa ndi katundu wako. 15 Anthu a ku Dedani+ ankachita nawe malonda. Iwe unalemba ntchito anthu oti azikuchitira malonda mʼzilumba zambiri. Anthuwo ankakupatsa minyanga+ komanso mitengo ya phingo ngati mphatso.* 16 Edomu ankachita nawe malonda chifukwa chakuti unali ndi katundu wochuluka. Anakupatsa miyala ya nofeki, ubweya wa nkhosa wapepo, nsalu zopeta zamitundu yosiyanasiyana, nsalu zabwino kwambiri, miyala yamtengo wapatali ya korali ndi ya rube posinthanitsa ndi katundu wako.
17 Yuda komanso dziko la Isiraeli linachita nawe malonda. Anakupatsa tirigu wa ku Miniti,+ zakudya zapamwamba, uchi,+ mafuta ndi basamu+ posinthanitsa ndi katundu wako.+
18 Damasiko+ ankachita nawe malonda chifukwa choti unali ndi katundu komanso chuma chambiri. Ankakupatsa vinyo wa ku Heliboni komanso ubweya wa nkhosa wa ku Zahari posinthanitsa ndi katundu wako. 19 Vedani ndi Yavani akudera la Uzali anakupatsa ziwiya zachitsulo, mitengo ya kasiya* ndi mabango onunkhira posinthanitsa ndi katundu wako. 20 Dedani+ ankachita nawe malonda a nsalu zoika pazishalo za mahatchi. 21 Unalemba ntchito Aluya ndi atsogoleri onse a ku Kedara,+ amene ankagulitsa ana a nkhosa, nkhosa zamphongo ndi mbuzi.+ 22 Unkachita malonda ndi amalonda a ku Sheba ndi ku Raama.+ Iwo anakupatsa mafuta onunkhira abwino kwambiri amitundu yosiyanasiyana, miyala yamtengo wapatali komanso golide posinthanitsa ndi katundu wako.+ 23 Harana,+ Kane, Edeni,+ amalonda a ku Sheba,+ Ashuri+ ndi Kilimadi ankachita nawe malonda. 24 Mʼmisika yako iwo ankachita malonda a zovala zokongola kwambiri, malaya opangidwa ndi nsalu yabuluu komanso nsalu yopeta yamitundu yosiyanasiyana ndi makapeti okhala ndi mitundu yosiyanasiyana. Zinthu zonsezi ankazimanga bwinobwino ndi zingwe.
25 Sitima zapamadzi za ku Tarisi+ zinkanyamula katundu wako wamalonda,
Choncho unali ndi chuma chambiri ndipo unalemera* pakati pa nyanja.
26 Anthu okupalasa akupititsa panyanja zozama.
Mphepo yakumʼmawa yakuwononga pakatikati pa nyanja.
27 Chuma chako, katundu wako, malonda ako, anthu amene akukuyendetsa, anthu ako oyenda panyanja,
anthu omata molumikizira matabwa ako, anthu amene amakugulitsira malonda+ komanso asilikali ako onse,+
Gulu lonse la anthu amene ali mwa iwe,*
Onsewo adzamira pakati pa nyanja pa tsiku limene udzawonongedwe.+
28 Anthu ako oyenda panyanja akadzafuula, madera amʼmphepete mwa nyanja adzagwedezeka.
29 Anthu onse opalasa ngalawa, oyendetsa sitima zapamadzi komanso anthu onse amene amagwira ntchito mʼsitima zapamadzi
Adzatsika mʼsitima zawo nʼkukaima pamtunda.
30 Iwo adzafuula ndipo adzakulirira mopwetekedwa mtima+
Uku akudzithira dothi kumutu kwawo komanso kudzigubuduza paphulusa.
31 Adzadzimeta mpala nʼkuvala ziguduli
Ndipo adzakulirira kwambiri komanso mopwetekedwa mtima.
32 Polira adzaimba nyimbo yoimba polira ndipo adzakuimbira kuti:
‘Ndi ndani angafanane ndi Turo, amene wawonongedwa* pakati pa nyanja?+
33 Katundu wako atabwera kuchokera pakatikati pa nyanja, unasangalatsa anthu ambiri.+
Chuma chako chochuluka komanso malonda ako zinalemeretsa mafumu apadziko lapansi.+
34 Tsopano wawonongeka pakatikati pa nyanja, mʼmadzi akuya,+
Ndipo katundu wako wamalonda komanso anthu ako amira nawe limodzi.+
35 Anthu onse amene akukhala mʼzilumba adzakuyangʼanitsitsa modabwa,+
Ndipo mafumu awo adzanjenjemera chifukwa cha mantha.+ Nkhope zawo zidzaoneka zankhawa.
36 Amalonda ochokera pakati pa mitundu ina ya anthu adzakuimbira mluzu chifukwa cha zimene zakuchitikira.
Mapeto ako adzafika modzidzimutsa ndipo adzakhala owopsa,
Moti sudzakhalaponso mpaka kalekale.’”’”+
28 Yehova anandiuzanso kuti: 2 “Iwe mwana wa munthu, uza mtsogoleri wa Turo kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti:
“Chifukwa chakuti wadzikuza mumtima mwako,+ ukumanena kuti, ‘Ndine mulungu.
Ndakhala pampando wachifumu wa mulungu pakatikati pa nyanja.’+
Koma ndiwe munthu basi, osati mulungu,
Ngakhale kuti mumtima mwako umadziona kuti ndiwe mulungu.
3 Iwe umaganiza kuti ndiwe wanzeru kuposa Danieli.+
Umaganiza kuti palibe chinsinsi chimene sukuchidziwa.
4 Chifukwa chakuti ndiwe wanzeru ndiponso wozindikira, walemera kwambiri,
Ndipo ukupitiriza kusonkhanitsa golide ndi siliva mʼnyumba zako zosungiramo chuma.+
5 Luso lako pa malonda linakubweretsera chuma chochuluka,+
Ndipo mtima wako unayamba kudzikuza chifukwa cha chuma chakocho.”’
6 ‘Choncho Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti:
“Chifukwa chakuti mumtima mwako umadziona kuti ndiwe mulungu,
7 Ine ndikubweretsa anthu ochokera mʼmayiko ena kuti adzakuukire, anthu ankhanza kwambiri a mitundu ina.+
Iwo adzasolola malupanga awo nʼkuwononga chilichonse chokongola chimene unapeza chifukwa cha nzeru zako
Ndipo adzaipitsa ulemerero wako waukulu.+
9 Kodi amene adzakuphe udzamuuzabe kuti, ‘Ine ndine mulungu?’
Kwa anthu amene adzakuipitse, iwe udzakhala munthu wamba, osati mulungu.”’
10 ‘Udzafa ngati anthu osadulidwa ndipo anthu amʼmayiko ena ndi amene adzakuphe,
Ine ndanena,’ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”
11 Yehova anandiuzanso kuti: 12 “Iwe mwana wa munthu, imba nyimbo yoimba polira yokhudza mfumu ya Turo. Uuze mfumuyo kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti:
13 Iwe unali mu Edeni, munda wa Mulungu.
Unakongoletsedwa ndi miyala yamtengo wapatali yamitundu yonse
Monga rube, topazi, yasipi, kulusolito, onekisi, yade, safiro, nofeki+ ndi emarodi.
Zoikamo miyala imeneyi zinali zagolide.
Ndinazipanga pa tsiku limene ndinakulenga.
14 Ine ndinakupatsa udindo kuti ukhale kerubi wodzozedwa amene amagwira ntchito yoteteza.
Unkakhala paphiri loyera la Mulungu+ ndipo unkayendayenda pakati pa miyala yamoto.
15 Unali wopanda cholakwa pa zochita zako kuchokera pa tsiku limene unalengedwa,
Mpaka pamene unayamba kuchita zinthu zosalungama.+
Choncho ndidzakuchotsa mʼphiri la Mulungu nʼkukuponya kunja monga wodetsedwa ndipo ndidzakuwononga.+
Iwe kerubi amene umagwira ntchito yoteteza, ndidzakuchotsa pakati pa miyala yamoto.
17 Mtima wako unadzikweza chifukwa cha kukongola kwako.+
Unawononga nzeru zako chifukwa cha ulemerero wako waukulu.+
Ndidzakuponyera kudziko lapansi,+
Ndipo mafumu azidzakuyangʼanitsitsa.
18 Iwe waipitsa malo ako opatulika chifukwa cha kuchuluka kwa zolakwa zako komanso malonda ako opanda chilungamo.
Ndidzachititsa kuti moto uyake pakati pako ndipo udzakupsereza.+
Ndidzakusandutsa phulusa padziko lapansi, pamaso pa anthu onse amene akukuyangʼana.
19 Onse amene ankakudziwa pakati pa mitundu ya anthu adzakuyangʼanitsitsa modabwa.+
Mapeto ako adzakhala odzidzimutsa komanso oopsa,
Ndipo sudzakhalaponso mpaka kalekale.”’”+
20 Yehova anandiuzanso kuti: 21 “Iwe mwana wa munthu, yangʼana ku Sidoni+ ndipo ulosere zoipa zimene zidzamuchitikire. 22 Unene kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti:
“Iwe Sidoni, ine ndikupatsa chilango ndipo ndidzalemekezedwa pakati pako.
Ndikadzapereka chiweruzo kwa iwe komanso ndikadzayeretsedwa kudzera mwa iwe, anthu adzadziwa kuti ine ndine Yehova.
23 Ndidzakutumizira mliri ndipo magazi adzayenderera mʼmisewu yako.
Anthu ambiri adzaphedwa pakati pako lupanga likadzabwera kudzakuukira kuchokera kumbali zonse,
Ndipo anthu adzadziwa kuti ine ndine Yehova.+
24 Zikadzatero, nyumba ya Isiraeli sidzazunguliridwanso ndi anthu amene amawanyoza, omwe ali ngati zitsamba zobaya komanso minga zaululu.+ Ndipo anthu adzadziwa kuti ine ndine Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”’
25 ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Ndikadzasonkhanitsanso pamodzi nyumba ya Isiraeli kuchokera kwa anthu a mitundu ina kumene anabalalikira,+ ndidzayeretsedwa pakati pawo pamaso pa mitundu ina ya anthu.+ Ndipo anthuwo adzakhala mʼdziko+ limene ndinapatsa mtumiki wanga Yakobo.+ 26 Adzakhala mʼdzikolo motetezeka+ ndipo adzamanga nyumba komanso kulima minda ya mpesa.+ Iwo azidzakhala motetezeka ndikadzapereka chiweruzo kwa onse owazungulira amene amawanyoza.+ Ndipo adzadziwa kuti ine ndine Yehova Mulungu wawo.”’”
29 Mʼchaka cha 10, mʼmwezi wa 10, pa tsiku la 12 la mweziwo, Yehova anandiuza kuti: 2 “Iwe mwana wa munthu, yangʼana kwa Farao mfumu ya Iguputo ndipo ulosere zoipa zimene zidzachitikire iyeyo ndi dziko lonse la Iguputo.+ 3 Umuuze kuti: ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti:
“Ine ndikulanga iwe Farao mfumu ya Iguputo,+
Iwe chilombo chachikulu chamʼnyanja chimene chagona mʼngalande zotuluka mumtsinje wake wa Nailo,+
Ndipo wanena kuti, ‘Mtsinje wa Nailo ndi wanga.
Ineyo ndinaupanga ndekha.’+
4 Koma ine ndidzakukola ndi ngowe munsagwada zako nʼkuchititsa kuti nsomba zamʼngalande za mtsinje wa Nailo zikakamire kumamba ako.
Ndidzakutulutsa mumtsinje wako wa Nailo pamodzi ndi nsomba zonse zamumtsinje wa Nailo zimene zakakamira kumamba ako.
5 Iwe pamodzi ndi nsomba zonse zamumtsinje wa Nailo ndidzakutayani mʼchipululu.
Mudzagwera panthaka yopanda chilichonse ndipo palibe amene adzakutengeni nʼkukakuikani mʼmanda.+
Ndidzakuperekani kwa zilombo zakutchire ndi mbalame zouluka mumlengalenga kuti mukhale chakudya chawo.+
6 Choncho anthu onse amene akukhala ku Iguputo adzadziwa kuti ine ndine Yehova,
Chifukwa sanalinso ngati ndodo yothandiza nyumba ya Isiraeli poyenda, koma anali ngati tsekera.*+
7 Atakugwira dzanja, unaphwanyika,
Ndipo unachititsa kuti athyole phewa lawo.
8 Choncho Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Ndibweretsa lupanga mʼdziko lako+ ndipo ndidzapha anthu ndi nyama zomwe. 9 Dziko la Iguputo lidzakhala malo owonongeka komanso bwinja.+ Iwo adzadziwa kuti ine ndine Yehova, chifukwa chakuti iwe wanena kuti,* ‘Mtsinje wa Nailo ndi wanga. Ineyo ndinaupanga ndekha.’+ 10 Choncho, iwe ndikulanga ndipo ndiwononga mtsinje wako wa Nailo ndipo dziko la Iguputo ndiliwononga nʼkulisandutsa malo ouma komanso bwinja,+ kuchokera ku Migidoli+ mpaka ku Seyene+ nʼkukafika kumalire a dziko la Itiyopiya. 11 Ndipo munthu kapena chiweto sichidzadutsa mʼdziko lako,+ ndipo simudzakhala munthu aliyense kwa zaka 40. 12 Ndidzachititsa kuti dziko la Iguputo likhale lowonongeka kwambiri kuposa mayiko ena onse, ndipo mizinda yake idzakhala yowonongeka kwambiri pa mizinda yonse kwa zaka 40.+ Ndidzamwaza Aiguputo pakati pa anthu a mitundu ina ndipo ndidzawabalalitsira mʼmayiko ena.”+
13 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Zaka 40 zikadzatha, ndidzasonkhanitsanso Aiguputowo nʼkuwabwezera kudziko lawo kuchokera kwa anthu a mitundu ina kumene anabalalikira.+ 14 Aiguputo amene anagwidwa nʼkupita nawo kudziko lina ndidzawabwezeretsa ku Patirosi,+ mʼdziko limene anachokera ndipo kumeneko Iguputo adzakhala ufumu wonyozeka. 15 Ufumu wa Iguputo udzakhala wochepa mphamvu kusiyana ndi maufumu ena ndipo sudzalamuliranso mitundu ina ya anthu.+ Ine ndidzawachepetsa kwambiri moti sadzathanso kugonjetsa mitundu ina ya anthu.+ 16 Nyumba ya Isiraeli sidzadaliranso ufumu umenewu.+ Koma udzangowakumbutsa zolakwa zimene anachita podalira Aiguputo kuti awathandize. Ndipo adzadziwa kuti ine ndine Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”’”
17 Tsopano mʼchaka cha 27, mʼmwezi woyamba, pa tsiku loyamba la mweziwo, Yehova analankhula nane kuti: 18 “Iwe mwana wa munthu, Nebukadinezara*+ mfumu ya Babulo anachititsa kuti asilikali ake agwire ntchito yaikulu pomenyana ndi Turo.+ Mutu wa msilikali aliyense unameteka ndipo mapewa awo ananyuka. Koma mfumuyo ndi asilikali akewo sanalandire malipiro aliwonse pa ntchito imene anagwira pomenyana ndi Turo.
19 Choncho Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Ine ndikupereka dziko la Iguputo kwa Nebukadinezara* mfumu ya Babulo.+ Iye adzatenga chuma cha dzikolo komanso kulanda zinthu zake zochuluka. Zimenezi zidzakhala malipiro a asilikali ake.
20 Ndimupatsa dziko la Iguputo monga chipukutamisozi pa ntchito imene anagwira pomenyana ndi Turo, chifukwa iwo anachita zimene ine ndinkafuna,’+ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.
21 Pa tsiku limenelo, ndidzaphukitsira nyumba ya Isiraeli nyanga*+ ndipo iwe ndidzakupatsa mpata kuti ulankhule pakati pawo, ndipo iwo adzadziwa kuti ine ndine Yehova.”
30 Yehova anandiuzanso kuti: 2 “Iwe mwana wa munthu, losera kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti:
“Lirani mofuula kuti, ‘Mayo ine, Tsiku lija likubwera!’
3 Tsikulo lili pafupi, inde tsiku la Yehova lili pafupi.+
Tsikulo lidzakhala la mitambo+ ndiponso nthawi yoikidwiratu yoti mitundu ya anthu iweruzidwe.+
4 Lupanga lidzabwera kudzaukira Iguputo, ndipo anthu a ku Itiyopiya adzachita mantha kwambiri anthu akadzaphedwa ku Iguputo.
Chuma cha Iguputo chidzalandidwa ndipo maziko ake adzagwetsedwa.+
5 Itiyopiya,+ Puti,+ Ludi, anthu onse ochokera mʼmitundu yosiyanasiyana,
Kubi limodzi ndi anthu amʼdziko lapangano,*
Onsewa adzaphedwa ndi lupanga.”’
6 Yehova wanena kuti:
‘Anthu amene akuthandiza Iguputo nawonso adzaphedwa,
Ndipo mphamvu zimene amazinyadira zidzatha.+
Anthu adzaphedwa ndi lupanga mʼdzikolo kuchokera ku Migidoli+ mpaka ku Seyene,’+ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. 7 ‘Onsewo adzawonongeka kwambiri pa mayiko onse ndipo mizinda yawo idzakhala yowonongeka kwambiri pa mizinda yonse.+ 8 Ndikadzayatsa moto mu Iguputo komanso ndikadzaphwanya onse amene akuthandizana nawo, iwo adzadziwa kuti ine ndine Yehova. 9 Pa tsikulo, ndidzatumiza amithenga pasitima zapamadzi kuti akaopseze Itiyopiya yemwe ndi wodzidalira. Itiyopiya adzachita mantha kwambiri pa tsiku limene Iguputo adzawonongedwe, chifukwa tsikulo lidzafika ndithu.’
10 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: ‘Ndidzawononga magulu a anthu a ku Iguputo pogwiritsa ntchito dzanja la Nebukadinezara,* mfumu ya Babulo.+ 11 Mfumuyo ndi asilikali ake, omwe ndi ankhanza kwambiri pa mayiko onse,+ adzabweretsedwa kuti adzawononge dzikolo. Iwo adzasolola malupanga awo nʼkuukira Iguputo ndipo adzadzaza dzikolo ndi anthu ophedwa.+ 12 Ndidzaumitsa ngalande zamumtsinje wa Nailo+ ndipo ndidzagulitsa dzikolo kwa anthu oipa. Ndidzachititsa kuti dzikolo ndi zonse zimene zili mmenemo ziwonongedwe ndi anthu ochokera kudziko lina.+ Ine Yehova, ndanena zimenezi.’
13 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: ‘Ndidzawononganso mafano onyansa* nʼkuthetsa milungu yopanda pake ya ku Nofi.*+ Sipadzapezekanso kalonga* wochokera mʼdziko la Iguputo ndipo ndidzachititsa kuti anthu amʼdzikolo azikhala mwamantha.+ 14 Mzinda wa Patirosi+ ndidzausandutsa bwinja. Mzinda wa Zowani ndidzauwotcha ndi moto ndipo ndidzaweruza mzinda wa No.*+ 15 Ndidzakhuthulira mkwiyo wanga pa Sini, mzinda umene Iguputo amaudalira kwambiri ndipo ndidzapha anthu ambiri a ku No. 16 Ndidzayatsa moto mu Iguputo. Sini adzachita mantha kwambiri ndipo adani adzagumula mpanda wa No nʼkulowa mumzindamo. Adani adzaukira mzinda wa Nofi* dzuwa likuswa mtengo. 17 Anyamata a ku Oni* ndi ku Pibeseti adzaphedwa ndi lupanga ndipo anthu amʼmizinda imeneyi adzatengedwa kupita ku ukapolo. 18 Mumzinda wa Tahapanesi mudzagwa mdima masana ndikadzathyola magoli a Iguputo kumeneko.+ Mphamvu zimene amanyadira zidzatha.+ Mitambo idzamuphimba ndipo anthu amʼmatauni ake adzatengedwa kupita ku ukapolo.+ 19 Ndidzapereka chiweruzo mu Iguputo ndipo iwo adzadziwa kuti ine ndine Yehova.’”
20 Ndiyeno mʼchaka cha 11, mʼmwezi woyamba, pa tsiku la 7 la mweziwo, Yehova anandiuza kuti: 21 “Iwe mwana wa munthu, ine ndathyola dzanja la Farao mfumu ya Iguputo. Dzanjalo silidzamangidwa kuti lichire kapena kukulungidwa ndi bandeji kuti likhale ndi mphamvu zoti nʼkugwira lupanga.”
22 “Choncho Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: ‘Ine ndilanga Farao mfumu ya Iguputo+ ndipo ndidzathyola manja ake onse, dzanja lamphamvu ndi lothyoka lomwe.+ Ndidzachititsa kuti lupanga ligwe mʼdzanja lake.+ 23 Kenako ndidzabalalitsira Aiguputo ku mitundu ina ya anthu nʼkuwamwaza mʼmayiko ena.+ 24 Ndidzalimbitsa manja a mfumu* ya Babulo+ ndipo ndidzaipatsa lupanga langa.+ Ndidzathyola manja a Farao ndipo adzabuula kwambiri ngati munthu amene watsala pangʼono kufa pamaso pa mfumu ya Babulo. 25 Ndidzalimbitsa manja a mfumu ya Babulo koma manja a Farao adzafooka. Ndikadzapereka lupanga langa mʼmanja mwa mfumu ya Babulo, iye nʼkuligwiritsa ntchito pomenyana ndi dziko la Iguputo,+ iwo adzadziwa kuti ine ndine Yehova. 26 Ine ndidzabalalitsira Aiguputo ku mitundu ina ya anthu nʼkuwamwaza mʼmayiko ena+ ndipo iwo adzadziwa kuti ine ndine Yehova.’”
31 Mʼchaka cha 11, mʼmwezi wachitatu, pa tsiku loyamba la mweziwo, Yehova anandiuzanso kuti: 2 “Iwe mwana wa munthu, uza Farao mfumu ya Iguputo ndi magulu a anthu amene amamutsatira+ kuti,
‘Kodi ndi ndani amene ali wamphamvu ngati iwe?
3 Iwe uli ngati Msuri, mtengo wa mkungudza wa ku Lebanoni,
Wa nthambi zokongola ngati ziyangoyango za masamba ambiri, mtengo wautali kwambiri,
Umene nsonga yake inafika mʼmitambo.
4 Mtengowo unakula kwambiri chifukwa cha madzi. Akasupe ozama anachititsa kuti mtengowo utalike.
Pamalo amene mtengowo unadzalidwa panali mitsinje yambiri yamadzi.
Ngalande za madziwo zinkathirira mitengo yonse yamʼmundamo.
5 Nʼchifukwa chake mtengowo unatalika kwambiri kuposa mitengo yonse yamʼmundamo.
Nthambi zake zinachuluka komanso zinatalika
Chifukwa cha kuchuluka kwa madzi mʼmitsinje yake.
6 Mbalame zonse zouluka mumlengalenga zinkamanga zisa zawo mʼnthambi zake,
Nyama zonse zakutchire zinkaberekera pansi pa nthambi zake,
Ndipo mitundu yonse ya anthu ambiri inkakhala mumthunzi wake.
7 Mtengowo unakhala wokongola kwambiri ndipo nthambi zake zinatalika kwambiri,
Chifukwa chakuti mizu yake inapita pansi nʼkukafika pamadzi ambiri.
8 Mitengo ina ya mkungudza sinafanane ndi mtengo umenewu mʼmunda wa Mulungu.+
Panalibe mtengo uliwonse wa junipa* umene unali ndi nthambi ngati zake,
Panalibe mtengo uliwonse wa katungulume umene nthambi zake zinali zofanana ndi za mtengowo.
Panalibenso mtengo wina mʼmunda wa Mulungu umene unali wokongola ngati mtengo umenewu.
9 Mtengo umenewu ndinaukongoletsa pouchulukitsira masamba,
Ndipo mitengo ina yonse ya mu Edeni, munda wa Mulungu woona, inkauchitira nsanje.’
10 Choncho Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: ‘Chifukwa chakuti mtengowu* unatalika kwambiri moti nsonga yake inakafika mʼmitambo, ndipo mtima wake unayamba kudzikuza chifukwa cha kutalika kwake, 11 ndidzaupereka mʼmanja mwa wolamulira wamphamvu wa anthu a mitundu ina.+ Iye adzaukhaulitsa ndithu, ndipo ine ndidzaukana chifukwa cha kuipa kwake. 12 Anthu amʼmayiko ena, mitundu ya anthu yankhanza kwambiri, adzadula mtengowo ndipo adzausiya mʼmapiri. Masamba ake adzagwera mʼzigwa zonse ndipo nthambi zake zidzathyoka nʼkugwera mʼmitsinje yonse yamʼdzikolo.+ Mitundu yonse ya anthu apadziko lapansi idzachoka mumthunzi wake nʼkuusiya. 13 Mbalame zonse zouluka mumlengalenga zizidzakhala pamtengo umene unagwetsedwawo, ndipo nyama zonse zakutchire zizidzakhala munthambi zake.+ 14 Zidzakhala choncho kuti pasadzapezekenso mtengo uliwonse umene uli pafupi ndi madzi, womwe udzatalike kwambiri kapena umene nsonga zake zidzafike mʼmitambo. Komanso kuti mtengo uliwonse umene uli pamadzi ambiri usadzatalike kukafika mʼmitambo. Chifukwa mitengo yonse idzafa nʼkutsikira pansi pa nthaka pamodzi ndi ana a anthu amene akutsikira kudzenje.’*
15 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: ‘Pa tsiku limene mtengowo udzatsikire ku Manda,* ndidzachititsa kuti anthu alire. Choncho ndidzaphimba madzi akuya komanso kutseka mitsinje yake kuti madzi ambiri asamadutse. Ndidzachititsa mdima mu Lebanoni chifukwa cha mtengowo ndipo mitengo yonse yakutchire idzafota. 16 Phokoso la kugwa kwake likadzamveka, ndidzachititsa kuti mitundu ya anthu injenjemere ndikamadzatsitsira mtengowo ku Manda* pamodzi ndi onse amene akutsikira kudzenje.* Ndipo mitengo yonse ya mu Edeni+ komanso mitengo yonse yabwino kwambiri ya ku Lebanoni imene ili pamadzi ambiri, idzatonthozedwa pansi pa nthaka. 17 Mitengo imeneyi yatsikira ku Manda* pamodzi ndi mtengo wa mkungudzawo. Yatsikira kwa ophedwa ndi lupanga+ limodzi ndi amene ankamuthandiza* omwe ankakhala mumthunzi wake pakati pa mitundu ina ya anthu.’+
18 ‘Kodi ndi mtengo uti pakati pa mitengo ya mu Edeni umene unkafanana ndi iwe pa nkhani ya ulemerero ndi kukula?+ Koma ndithu udzafa* limodzi ndi mitengo ya mu Edeni. Udzagona pakati pa anthu osadulidwa limodzi ndi ophedwa ndi lupanga. Mtengo umenewu ukuimira Farao ndi magulu onse a anthu amene amamutsatira,’ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”
32 Mʼchaka cha 12, mʼmwezi wa 12, pa tsiku loyamba la mweziwo, Yehova anandiuzanso kuti: 2 “Iwe mwana wa munthu, imba nyimbo yoimba polira yokhudza Farao, mfumu ya Iguputo ndipo umuuze kuti,
‘Iwe unali ngati mkango waungʼono wamphamvu* wa mitundu ina ya anthu,
Koma wakhalitsidwa chete.
Unali ngati chilombo chamʼnyanja+ chimene chimavundula madzi mwamphamvu mʼmitsinje yako
Nʼkumadetsa madzi ndi mapazi ako ndiponso kuipitsa mitsinjeyo.’
3 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti:
‘Ndidzakuphimba ndi ukonde wanga pogwiritsa ntchito anthu a mitundu ina amene asonkhana pamodzi,
Ndipo iwo adzakukoka ndi khoka langa.
4 Ndidzakusiya pamtunda
Ndiponso ndidzakuponya pabwalo.
Ndidzachititsa kuti mbalame zonse zouluka mumlengalenga zitere pa iwe,
Ndipo ndidzakhutitsa zilombo zapadziko lonse lapansi ndi nyama yako.+
6 Ndidzanyowetsa dziko ndi magazi amene akutuluka mwamphamvu mʼthupi mwako mpaka kumapiri,
Ndipo adzadzaza mitsinje.
7 Ndikadzakuzimitsa, ndidzaphimba kumwamba nʼkuchititsa mdima nyenyezi zake.
Dzuwa ndidzaliphimba ndi mitambo,
Ndipo mwezi sudzaonetsa kuwala kwake.+
8 Zounikira zonse zakumwamba ndidzazichititsa mdima chifukwa cha iwe,
Ndipo ndidzagwetsa mdima mʼdziko lako,’ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.
9 ‘Ndidzachititsa kuti mitima ya anthu ambiri ikhale ndi nkhawa ndikadzatenga anthu ako ogwidwa ukapolo nʼkuwapititsa kwa anthu a mitundu ina,
Kumayiko amene sukuwadziwa.+
10 Ndidzachititsa mantha anthu ambiri a mitundu ina,
Ndipo mafumu awo adzanjenjemera ndi mantha chifukwa cha iwe ndikadzawaloza ndi lupanga langa.
Iwo azidzanjenjemera mosalekeza chifukwa choopa kufa,
Pa tsiku limene udzaphedwe.’
11 Chifukwa Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti:
‘Lupanga la mfumu ya Babulo lidzakuukira.+
12 Ndidzachititsa kuti gulu la anthu amene amakutsatira aphedwe ndi malupanga a asilikali amphamvu.
Onsewo ndi anthu a mitundu ina omwe ndi ankhanza kwambiri.+
Iwo adzawononga zinthu zimene Iguputo amazinyadira ndipo anthu ambiri amene amamutsatira adzaphedwa.+
13 Ndidzawononga ziweto zake zonse zimene zili mʼmbali mwa madzi ambiri.+
Ndipo phazi la munthu kapena ziboda za ziweto sizidzadetsanso madziwo.+
14 Pa nthawi imeneyo ndidzayeretsa madzi awo,
Ndipo ndidzachititsa kuti madzi amʼmitsinje yawo ayende ngati mafuta,’ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.
15 ‘Ndikadzachititsa kuti dziko la Iguputo likhale bwinja, dziko limene zinthu zake zonse zalandidwa,+
Ndikadzapha anthu onse amene akukhala mʼdzikolo,
Iwo adzadziwa kuti ine ndine Yehova.+
16 Imeneyi ndi nyimbo yoimba polira ndipo anthu adzaiimba.
Ana aakazi a mitundu ina ya anthu adzaiimba.
Nyimbo imeneyi adzaimbira Iguputo ndi gulu la anthu onse amene amamutsatira,’ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”
17 Kenako mʼchaka cha 12, pa tsiku la 15 la mwezi, Yehova anandiuzanso kuti: 18 “Iwe mwana wa munthu, lirira gulu la anthu onse a ku Iguputo ndipo utsitsire dzikolo kumanda. Utsitsire kumanda dzikolo ndi ana aakazi a mitundu yamphamvu limodzi ndi amene akutsikira kudzenje.*
19 ‘Kodi ndiwe wokongola kuposa ndani? Tsikira kumanda ndipo ukagone limodzi ndi anthu osadulidwa.
20 Iguputo adzaphedwa pamodzi ndi anthu amene aphedwa ndi lupanga.+ Iye adzaphedwa ndi lupanga. Mukokereni kutali limodzi ndi gulu la anthu ake onse amene amamutsatira.
21 Ali pansi pa Manda,* asilikali amphamvu kwambiri adzalankhula ndi iyeyo komanso amene ankamuthandiza. Onsewo adzatsikira kumanda ndipo adzagona limodzi ndi anthu osadulidwa, ataphedwa ndi lupanga. 22 Asuri ali kumeneko limodzi ndi gulu lake lonse. Manda a anthu a ku Asuri ali mozungulira mfumu yawo. Onsewo anaphedwa ndi lupanga.+ 23 Manda a Asuri ali pakatikati pa dzenje ndipo gulu lake lonse lazungulira manda akewo. Onsewo anaphedwa ndi lupanga chifukwa anachititsa kuti anthu amene akukhala mʼdziko la anthu amoyo azikhala mwamantha.
24 Elamu+ ali kumandako limodzi ndi gulu la anthu ake onse amene ankamutsatira ndipo anthuwo azungulira manda ake. Onsewo anaphedwa ndi lupanga. Iwo anatsikira kunthaka ali osadulidwa. Anthu amenewa anachititsa kuti anthu amene akukhala mʼdziko la anthu amoyo azikhala mwamantha. Tsopano anthu amenewa adzachita manyazi limodzi ndi anthu amene akutsikira kudzenje.* 25 Iwo amupangira bedi pakati pa anthu amene aphedwa limodzi ndi gulu la anthu ake onse amene ankamutsatira, onse azungulira manda ake. Onsewo ndi anthu osadulidwa, amene aphedwa ndi lupanga chifukwa anachititsa kuti anthu amene akukhala mʼdziko la anthu amoyo azikhala mwamantha. Iwo adzachita manyazi limodzi ndi anthu amene akutsikira kudzenje.* Iye waikidwa mʼmanda pakati pa anthu ophedwa.
26 Kumeneko nʼkumene kuli Meseki ndi Tubala+ limodzi ndi magulu a anthu awo onse amene ankawatsatira. Manda awo ali mozungulira mfumu yawo. Onsewa ndi anthu osadulidwa, anthu amene anabaidwa ndi lupanga chifukwa anachititsa kuti anthu amene akukhala mʼdziko la anthu amoyo azikhala mwamantha. 27 Kodi amenewa sadzagona limodzi ndi asilikali amphamvu osadulidwa amene anaphedwa, amene anatsikira ku Manda* limodzi ndi zida zawo zankhondo? Iwo adzaika malupanga awo pansi pa mitu yawo* ndipo machimo awo adzawaika pamafupa awo chifukwa asilikali amphamvuwo anawononga dziko la anthu amoyo. 28 Koma iwe udzaphwanyidwa pakati pa anthu osadulidwa ndipo udzagona limodzi ndi anthu amene anaphedwa ndi lupanga.
29 Edomu+ ali kumeneko. Kulinso mafumu ake ndi atsogoleri ake onse amene ngakhale kuti anali amphamvu, anaikidwa mʼmanda limodzi ndi anthu amene anaphedwa ndi lupanga. Anthu amenewanso adzagona limodzi ndi anthu osadulidwa+ komanso anthu amene akutsikira kudzenje.*
30 Kumeneko kuli akalonga* onse akumpoto limodzi ndi Asidoni onse+ amene anatsikira kumanda ali amanyazi. Anatsikira kumeneko limodzi ndi anthu amene anaphedwa, ngakhale kuti anali ochititsa mantha chifukwa cha mphamvu zawo. Adzagona mʼmanda ali osadulidwa limodzi ndi anthu amene anaphedwa ndi lupanga ndipo adzachita manyazi limodzi ndi anthu amene akutsikira kudzenje.*
31 Farao adzaona zinthu zonsezi ndipo mtima wake udzakhala mʼmalo chifukwa cha zonse zimene zinachitikira gulu la anthu amene ankamutsatira.+ Farao ndi asilikali ake onse adzaphedwa ndi lupanga,’ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.
32 ‘Chifukwa anachititsa kuti anthu amene akukhala mʼdziko la anthu amoyo azikhala mwamantha, Farao ndi gulu lonse la anthu amene ankamutsatira adzaikidwa mʼmanda limodzi ndi anthu osadulidwa. Adzaikidwa mʼmanda pamodzi ndi anthu amene anaphedwa ndi lupanga,’ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”
33 Yehova anandiuza kuti: 2 “Iwe mwana wa munthu, lankhula ndi anthu a mtundu wako+ ndipo uwauze kuti,
‘Tiyerekeze kuti ndabweretsa lupanga mʼdziko,+ ndiyeno anthu onse amʼdzikolo asankha munthu kuti akhale mlonda wawo, 3 ndiye mlondayo waona lupanga likubwera kudzaukira dzikolo, nʼkuliza lipenga la nyanga ya nkhosa kuchenjeza anthu.+ 4 Ngati munthu wamva kulira kwa lipenga koma osamvera chenjezolo,+ lupanga nʼkubwera ndi kumupha, magazi ake adzakhala pamutu pake.+ 5 Iye anamva kulira kwa lipenga koma sanamvere chenjezolo. Magazi ake adzakhala pamutu pake. Akanamvera chenjezolo, akanapulumutsa moyo wake.
6 Ngati mlondayo waona lupanga likubwera, koma iye osaliza lipenga,+ anthu osamva chenjezo lililonse, lupangalo nʼkufika ndi kupha munthu, munthuyo adzafa chifukwa cha zolakwa zake, koma mlondayo ndidzamuimba mlandu chifukwa cha imfa ya munthuyo.’*+
7 Koma iwe mwana wa munthu, ine ndakuika kuti ukhale mlonda wa nyumba ya Isiraeli. Choncho ukamva mawu ochokera pakamwa panga ukuyenera kuwachenjeza.+ 8 Ndikauza munthu woipa kuti, ‘Munthu woipa iwe, udzafa ndithu,’+ koma iwe osanena chilichonse pochenjeza woipayo kuti asinthe zochita zake, iyeyo adzafa monga munthu woipa chifukwa cha zolakwa zake,+ koma iwe ndidzakuimba mlandu chifukwa cha magazi ake.* 9 Koma iwe ukachenjeza munthu woipa kuti asiye zinthu zoipa zimene akuchita, iye nʼkukana kusiya zoipazo, munthuyo adzafa chifukwa cha zolakwa zake,+ koma iweyo udzapulumutsa moyo wako ndithu.+
10 Ndiye iwe mwana wa munthu, uza nyumba ya Isiraeli kuti, ‘Inu mwanena kuti: “Kupanduka kwathu komanso machimo athu zikutilemera kwambiri, nʼkutichititsa kuti titope kwambiri.+ Ndiye tingapitirize bwanji kukhala ndi moyo?”’+ 11 Auze kuti, ‘“Pali ine Mulungu wamoyo,” akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, “Ine sindisangalala ndi imfa ya munthu woipa,+ koma ndimafuna kuti munthu woipa asinthe zochita zake+ nʼkupitiriza kukhala ndi moyo.+ Bwererani! Bwererani nʼkusiya zinthu zoipa zimene mukuchita.+ Muferenji inu a nyumba ya Isiraeli?”’+
12 Iwe mwana wa munthu, uza anthu a mtundu wako kuti, ‘Munthu wolungama akapanduka, zinthu zolungama zimene ankachita, sizidzamupulumutsa.+ Munthu woipa akasiya zoipa zakezo, zoipazo sizidzachititsa kuti apunthwe.+ Komanso pa tsiku limene munthu wolungama wachimwa, zinthu zolungama zimene ankachita zija sizidzamuthandiza kuti apitirize kukhala ndi moyo.+ 13 Ndikauza munthu wolungama kuti: “Ndithu, iwe udzapitiriza kukhala ndi moyo,” ndiyeno iyeyo nʼkuyamba kukhulupirira kuti zinthu zolungama zimene anachita mʼmbuyo zidzamupulumutsa nʼkuchita zinthu zoipa,*+ zinthu zonse zolungama zimene anachita zija sizidzakumbukiridwa. Iye adzafa chifukwa cha zinthu zoipa zimene wachita.+
14 Ndikauza munthu woipa kuti: “Udzafa ndithu,” ndiyeno iyeyo nʼkusiya machimo akewo, nʼkuyamba kuchita zinthu motsatira malamulo ndiponso mwachilungamo,+ 15 komanso munthu woipayo akabweza chinthu chimene anatenga kwa munthu amene anakongola zinthu zake,+ akabweza zinthu zimene analanda mwauchifwamba,+ nʼkuyamba kuyenda motsatira malamulo opatsa moyo popewa kuchita zinthu zoipa, ndithu munthuyo adzapitiriza kukhala ndi moyo.+ Iye sadzafa. 16 Sadzapatsidwa chilango chifukwa cha machimo amene anachitawo.+ Adzapitiriza kukhala ndi moyo chifukwa chochita zinthu motsatira malamulo ndiponso mwachilungamo.’+
17 Koma anthu a mtundu wako anena kuti, ‘Njira za Yehova nʼzopanda chilungamo,’ pamene njira zawo ndi zimene zili zopanda chilungamo.
18 Munthu amene amachita zinthu zabwino akasiya kuchita zabwinozo nʼkumachita zoipa,* akuyenera kufa chifukwa cha zochita zakezo.+ 19 Koma munthu woipa akasiya kuchita zinthu zoipa nʼkuyamba kuchita zinthu motsatira malamulo ndiponso mwachilungamo, adzapitiriza kukhala ndi moyo chifukwa chochita zimenezi.+
20 Koma inu mwanena kuti, ‘Njira za Yehova nʼzopanda chilungamo.’+ Inu a nyumba ya Isiraeli, ine ndidzaweruza aliyense wa inu mogwirizana ndi zochita zake.”
21 Patapita nthawi, mʼchaka cha 12, mʼmwezi wa 10, tsiku la 5 la mweziwo, kuchokera pamene tinatengedwa kupita ku ukapolo, munthu wina amene anathawa ku Yerusalemu anabwera kwa ine+ nʼkundiuza kuti: “Mzinda uja wawonongedwa!”+
22 Ndiyeno madzulo, munthu amene anathawa uja asanafike, dzanja la Yehova linandikhudza ndipo Mulungu anatsegula pakamwa panga munthu uja asanafike mʼmawa. Choncho pakamwa panga panatseguka ndipo ndinayambanso kulankhula.+
23 Kenako Yehova anandiuza kuti: 24 “Iwe mwana wa munthu, anthu amene akukhala mʼmabwinjawa+ akulankhula zokhudza dziko la Isiraeli kuti, ‘Abulahamu anali munthu mmodzi, koma anatenga dzikoli kukhala lake.+ Ife tilipo ambiri, choncho dzikoli laperekedwa kwa ife kuti likhale lathu.’
25 Choncho auze kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Inu mukudya nyama limodzi ndi magazi ake,+ mumadalira* mafano anu onyansa* ndipo mukupitiriza kukhetsa magazi.+ Ndiye pamenepa ndinu oyenera kutenga dzikoli kuti likhale lanu? 26 Inu mukudalira lupanga lanu,+ mukuchita zinthu zonyansa ndipo aliyense wa inu akugona ndi mkazi wa mnzake.+ Ndiye kodi pamenepa ndinu oyenera kutenga dzikoli kuti likhale lanu?”’+
27 Uwauze kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Pali ine Mulungu wamoyo, anthu amene akukhala mʼmabwinja adzaphedwa ndi lupanga. Amene ali kutchire ndidzawapereka kwa zilombo zolusa kuti akhale chakudya chawo. Ndipo amene ali mʼmalo otetezeka komanso mʼmapanga adzafa ndi matenda.+ 28 Ndidzachititsa kuti dzikolo likhale bwinja lowonongeka kwambiri.+ Ndidzathetsa kudzikuza komanso kunyada kwake ndipo mapiri a mu Isiraeli adzawonongedwa+ moti sipadzapezeka wodutsamo. 29 Ndikadzachititsa kuti dzikolo likhale bwinja lowonongeka kwambiri+ chifukwa cha zinthu zonse zonyansa zimene achita, iwo adzadziwa kuti ine ndine Yehova.”’+
30 Koma iwe mwana wa munthu, anthu a mtundu wako akukambirana za iwe mʼmbali mwa mpanda komanso mʼmakomo a nyumba.+ Aliyense akuuza mʼbale wake kuti, ‘Bwerani tidzamve mawu ochokera kwa Yehova.’ 31 Iwo adzasonkhana nʼkukhala pamaso pako ngati anthu anga. Adzamva mawu ako koma sadzawatsatira.+ Chifukwa ndi pakamwa pawo, amakuuza zongofuna kukusangalatsa,* koma mtima wawo ukungofuna kupeza phindu mwachinyengo. 32 Kwa iwo uli ngati nyimbo yachikondi imene yaimbidwa mwaluso ndi choimbira cha zingwe komanso ndi mawu anthetemya. Iwo adzamva mawu ako, koma palibe amene adzawatsatire. 33 Koma mawu ako akadzakwaniritsidwa, chifukwa adzakwaniritsidwa ndithu, iwo adzadziwa kuti pakati pawo panali mneneri.”+
34 Yehova anandiuzanso kuti: 2 “Iwe mwana wa munthu, losera zoipa zimene zidzachitikire abusa a Isiraeli. Losera ndipo uuze abusawo kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Tsoka abusa a Isiraeli,+ amene akhala akungodzidyetsa okha! Kodi abusa ntchito yawo si kudyetsa nkhosa?+ 3 Inu mukudya mafuta, ndipo mukuvala zovala zaubweya wa nkhosa. Mukupha nyama zonenepa kwambiri,+ koma nkhosa simukuzidyetsa.+ 4 Nkhosa zofooka simunazilimbitse ndipo zodwala simunazichiritse. Zovulala simunazimange. Nkhosa zosochera simunazibweze ndipo zimene zasowa simunazifufuze.+ Koma munkazilamulira mwankhanza komanso mopondereza.+ 5 Choncho zinamwazikana chifukwa zinalibe mʼbusa+ ndipo zinakhala chakudya cha zilombo zonse zakutchire. 6 Nkhosa zanga zinasochera mʼmapiri onse ndi mʼzitunda zonse zitalizitali. Nkhosa zanga zinabalalika padziko lonse lapansi ndipo panalibe amene ankazifufuza kapena kuziyangʼanayangʼana.
7 Choncho abusa inu, imvani mawu a Yehova: 8 ‘“Pali ine Mulungu wamoyo,” akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, “nkhosa zanga zagwidwa ndipo zakhala chakudya cha zilombo zonse zakutchire chifukwa panalibe mʼbusa ndipo abusa anga sanazifunefune. Koma ankangodzidyetsa okha, osadyetsa nkhosa zanga.”’ 9 Choncho abusa inu, imvani mawu a Yehova. 10 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: ‘Ine nditsutsa abusawo ndipo ndiwauza kuti andibwezere nkhosa zanga. Ndiwaletsa kuti asamadyetse* nkhosa zanga+ ndipo abusawo sadzadzidyetsanso okha. Ndidzalanditsa nkhosa zanga mʼkamwa mwawo ndipo sizidzakhalanso chakudya chawo.’”
11 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Ine ndilipo ndipo ndidzafunafuna nkhosa zanga ndi kuzisamalira.+ 12 Ndidzasamalira nkhosa zanga ngati mʼbusa amene wapeza nkhosa zake zimene zinabalalika ndipo akuzidyetsa.+ Ndidzazipulumutsa mʼmalo onse amene zinabalalikira pa tsiku la mitambo ndi mdima wandiweyani.+ 13 Nkhosa zanga ndidzazitulutsa pakati pa anthu a mitundu ina. Ndidzazisonkhanitsa pamodzi kuchokera mʼmayiko ena nʼkuzibweretsa mʼdziko lawo. Ndidzazidyetsa mʼmapiri a ku Isiraeli,+ mʼmphepete mwa mitsinje komanso pafupi ndi malo onse amʼdzikolo kumene kumakhala anthu. 14 Nkhosazo ndidzazidyetsera mʼmalo a msipu wabwino ndipo malo amene zizidzadya msipu adzakhala kumapiri ataliatali a ku Isiraeli.+ Kumeneko zizidzagona pansi mʼmalo abwino kwambiri odyetserako ziweto+ ndipo zizidzadya msipu wabwino kwambiri mʼmapiri a ku Isiraeli.
15 Ine ndidzadyetsa nkhosa zanga+ ndipo ndidzazipatsa malo oti zigone,”+ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. 16 “Nkhosa imene yasowa ndidzaifunafuna,+ imene yasochera ndidzaibweza. Imene yavulala ndidzaimanga povulalapo ndipo imene ili yofooka ndidzailimbitsa, koma yonenepa ndi yamphamvu ndidzaiwononga. Ndidzaipatsa chiweruzo kuti chikhale chakudya chake.”
17 Ponena za inu nkhosa zanga, Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Ine ndatsala pangʼono kuweruza pakati pa nkhosa ndi nkhosa inzake komanso pakati pa nkhosa zamphongo ndi mbuzi zamphongo.+ 18 Kodi kudya msipu wabwino kwambiri si kokwanira kwa inu? Kodi mukuyeneranso kumapondaponda msipu wotsala ndi mapazi anu? Ndipo mukamaliza kumwa madzi oyera, kodi mukuyenera kuwadetsa powapondaponda ndi mapazi anu? 19 Kodi nkhosa zanga zizidya msipu umene inu mwaupondaponda ndi mapazi anu komanso kumwa madzi amene mwawadetsa powapondaponda ndi mapazi anu?”
20 Choncho Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wauza nkhosazo kuti: “Ine ndilipo ndipo ndidzapereka chiweruzo pakati pa nkhosa yonenepa ndi nkhosa yowonda. 21 Ndidzachita zimenezi chifukwa chakuti munkakankha nkhosa ndi nthiti zanu ndiponso mapewa anu. Ndipo munkagunda ndi nyanga zanu nkhosa zonse zodwala mpaka kuzibalalitsira kutali. 22 Ine ndidzapulumutsa nkhosa zanga, ndipo sizidzagwidwanso ndi zilombo.+ Ndidzaweruza pakati pa nkhosa ndi nkhosa inzake. 23 Ndidzazipatsa mʼbusa mmodzi+ amene ndi mtumiki wanga Davide,+ ndipo adzazidyetsa. Iye adzakhala mʼbusa wawo ndipo azidzazidyetsa.+ 24 Ine Yehova ndidzakhala Mulungu wawo,+ ndipo mtumiki wanga Davide adzakhala mtsogoleri pakati pawo.+ Ine Yehova ndanena zimenezi.
25 Ine ndidzachita pangano lamtendere ndi nkhosazo.+ Ndipo ndidzachotsa zilombo zolusa mʼdzikomo+ nʼcholinga choti nkhosazo zizidzakhala mʼchipululu zili zotetezeka ndipo zizidzagona munkhalango.+ 26 Nkhosazo komanso malo ozungulira phiri langa adzalandira madalitso+ ndipo ndidzachititsa kuti mvula igwe pa nthawi yake. Madalitso adzagwa ambiri ngati mvula.+ 27 Mitengo yamʼdzikomo idzabereka zipatso ndipo nthaka idzatulutsa zokolola zake.+ Iwo adzakhala mʼdzikolo motetezeka ndipo adzadziwa kuti ine ndine Yehova ndikadzathyola goli lawo+ nʼkuwapulumutsa kwa anthu amene anawagwira kuti akhale akapolo awo. 28 Anthu a mitundu ina sadzawagwiranso ndipo zilombo zolusa sizidzawadya. Iwo azidzakhala motetezeka popanda aliyense wowaopseza.+
29 Ndidzawapatsa munda umene udzakhale wotchuka* chifukwa cha mbewu zake ndipo anthu sadzafanso ndi njala mʼdzikomo+ komanso anthu a mitundu ina sadzawanyozanso.+ 30 ‘Zikadzatero, iwo adzadziwa kuti ine, Yehova Mulungu wawo, ndili nawo limodzi ndiponso kuti iwowo, a nyumba ya Isiraeli ndi anthu anga,’+ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”’
31 ‘Koma inu nkhosa zanga,+ nkhosa zimene ndikuzisamalira, ndinu anthu basi ndipo ine ndine Mulungu wanu,’ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”
35 Yehova anandiuzanso kuti: 2 “Iwe mwana wa munthu, yangʼana dera lamapiri la Seiri+ ndipo ulosere zoipa zimene zidzachitikire deralo.+ 3 Uuze deralo kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Iwe dera lamapiri la Seiri, ine ndikupatsa chilango. Nditambasula dzanja langa nʼkukukhaulitsa ndipo ndikusandutsa bwinja lowonongeka kwambiri.+ 4 Mizinda yako ndidzaisandutsa bwinja komanso udzakhala malo owonongeka kwambiri+ ndipo udzadziwa kuti ine ndine Yehova. 5 Chifukwa chakuti unasonyeza chidani chachikulu+ ndipo unapha Aisiraeli ndi lupanga pa nthawi ya tsoka lawo, pamene ankalandira chilango chawo chomaliza.”’+
6 ‘Choncho pali ine Mulungu wamoyo,’ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, ‘Ndidzakonza zoti magazi ako akhetsedwe ndipo mlandu wa magazi udzakutsatira.+ Chifukwa unkadana ndi anthu amene unakhetsa magazi awo, mlandu wa magazi udzakutsatira.+ 7 Dera lamapiri la Seiri ndidzalisandutsa bwinja lowonongeka kwambiri+ ndipo ndidzawononga aliyense amene akudutsa kumeneko komanso aliyense wochokera kumeneko. 8 Mʼmapiri amʼderalo ndidzadzazamo anthu amene aphedwa ndipo anthu amene aphedwa ndi lupanga adzagwera mʼzitunda zako, mʼzigwa zako ndi mʼmitsinje yako yonse. 9 Ndidzakusandutsa malo omwe adzakhale owonongeka mpaka kalekale. Mʼmizinda yako simudzakhalanso anthu+ ndipo udzadziwa kuti ine ndine Yehova.’
10 Chifukwa unanena kuti, ‘Mitundu iwiri iyi ya anthu ndi mayiko awiri awa zidzakhala zanga ndipo ife tidzatenga zonsezi.’+ Unanena zimenezi ngakhale kuti Yehova anali komweko. 11 ‘Choncho pali ine Mulungu wamoyo,’ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, ‘Ndidzakulanga mogwirizana ndi mkwiyo komanso nsanje imene unaisonyeza chifukwa chakuti unkadana nawo,+ ndipo ndikadzakuweruza, iwo adzandidziwa. 12 Pa nthawi imeneyo udzadziwa kuti ine Yehova, ndinamva mawu onse achipongwe amene unanenera mapiri a ku Isiraeli. Pamene unanena kuti, “Mapiri aja awonongedwa ndipo aperekedwa kwa ife kuti tiwadye.”* 13 Iwe unalankhula modzitama kwa ine ndipo unachulukitsa mawu ako ondinyoza.+ Ine ndinamva zonsezo.’
14 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: ‘Dziko lonse lapansi lidzasangalala ndikadzakusandutsa bwinja lowonongeka kwambiri. 15 Mofanana ndi mmene unasangalalira cholowa cha nyumba ya Isiraeli chitawonongedwa, ine ndidzachitanso chimodzimodzi kwa iwe.+ Iwe dera lamapiri la Seiri, kutanthauza Edomu yense,+ udzasanduka bwinja, ndipo anthu adzadziwa kuti ine ndine Yehova.’”
36 “Koma iwe mwana wa munthu, losera zokhudza mapiri a ku Isiraeli ndipo unene kuti, ‘Inu mapiri a ku Isiraeli, imvani mawu a Yehova. 2 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Mdani wanu wakunenani kuti, ‘Eyaa! Ngakhale malo okwezeka akalekale tawatenga kuti akhale athu!’”’+
3 Choncho losera ndipo unene kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Adani anu akusandutsani bwinja ndipo akuukirani kuchokera kumbali zonse. Achita zimenezi kuti anthu a mitundu ina amene anapulumuka* akutengeni kuti mukhale awo ndipo anthu akunena za inu komanso kukunenerani miseche.+ 4 Choncho inu mapiri a ku Isiraeli, imvani mawu a Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wauza mapiri ndi zitunda, mitsinje ndi zigwa, mabwinja a malo amene anawonongedwa+ komanso mizinda yopanda anthu imene anthu a mitundu ina amene anapulumuka anaitenga kuti ikhale yawo. Anthuwo ankakhala moizungulira ndipo ankainyoza.+ 5 Mawu amene Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, akuwauza ndi akuti: ‘Ndidzadzudzula anthu a mitundu ina amene anapulumuka komanso Edomu yense nditakwiya kwambiri.+ Ndidzadzudzula amene anatenga dziko langa kuti likhale lawo akusangalala kwambiri komanso akunyoza+ nʼcholinga choti dzikolo ndi malo ake odyetserako ziweto zikhale zawo.’”’+
6 Choncho losera zokhudza dziko la Isiraeli ndipo uuze mapiri, zitunda, mitsinje ndi zigwa kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Ineyo ndidzalankhula mwaukali ndiponso nditakwiya kwambiri chifukwa chakuti anthu a mitundu ina akhala akukunyozani.”’+
7 Choncho Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: ‘Ine ndikulumbira nditakweza dzanja langa kuti mitundu imene yakuzungulirani idzachita manyazi.+ 8 Koma inu mapiri a Isiraeli, mudzatulutsa nthambi nʼkuberekera zipatso anthu anga Aisiraeli,+ chifukwa chakuti abwerera mʼdziko lawo posachedwapa. 9 Chifukwa ine ndili ndi inu ndipo ndidzakukomerani mtima moti anthu adzalima minda mwa inu nʼkudzala mbewu. 10 Ndidzachulukitsa anthu anu. Ndidzachulukitsa nyumba yonse ya Isiraeli. Anthu adzayamba kukhala mʼmizinda+ ndipo malo amene anali mabwinja adzamangidwanso.+ 11 Inde, ndidzachulukitsa anthu anu ndi ziweto zanu.+ Adzachuluka nʼkuberekana kwambiri. Ndidzachititsa kuti anthu akhale mwa inu ngati mmene zinalili poyamba+ ndipo ndidzachititsa kuti zinthu zikuyendereni bwino kwambiri kuposa poyamba.+ Choncho inu mudzadziwa kuti ine ndine Yehova.+ 12 Ndidzachititsa kuti anthu, anthu anga Aisiraeli, azidzayendayenda mwa inu ndipo adzakutengani kuti mukhale awo.+ Inu mudzakhala cholowa chawo ndipo simudzawalandanso ana awo.’”+
13 “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: ‘Anthu akukunenani kuti: “Inu ndinu dziko limene limadya anthu ndipo mumapha ana a mitundu ya anthu anu.”’ 14 ‘Pa chifukwa chimenechi inu simudzadyanso anthu kapena kuchititsa kuti mitundu ya anthu anu ikhale yopanda ana,’ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. 15 ‘Sindidzachititsanso kuti anthu a mitundu ina azikunyozani kapena kuti anthu azikunenerani mawu achipongwe+ ndipo simudzakhumudwitsanso mitundu ya anthu amene akukhala mwa inu,’ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”
16 Yehova anandiuzanso kuti: 17 “Iwe mwana wa munthu, pa nthawi imene a nyumba ya Isiraeli ankakhala mʼdziko lawo, analidetsa ndi makhalidwe awo komanso zochita zawo.+ Kwa ine, khalidwe lawo linali ngati zonyansa za mkazi amene akusamba.+ 18 Choncho ndinawakhuthulira mkwiyo wanga chifukwa cha magazi amene iwo anakhetsa mʼdzikoli+ komanso chifukwa chakuti anadetsa dzikoli ndi mafano awo onyansa.*+ 19 Ndiye ndinawabalalitsira kwa anthu a mitundu ina ndipo ndinawamwaza mʼmayiko osiyanasiyana.+ Ndinawaweruza mogwirizana ndi njira zawo komanso zochita zawo. 20 Koma atapita kwa anthu a mitundu inawo, anthuwo anadetsa dzina langa loyera+ ponena za iwowo kuti, ‘Awa ndi anthu a Yehova, koma anachoka mʼdziko lake.’ 21 Ndidzachita zinthu zosonyeza kuti ndikudera nkhawa dzina langa loyera, limene nyumba ya Isiraeli yalidetsa pakati pa anthu a mitundu ina kumene iwo anapita.”+
22 “Choncho uza nyumba ya Isiraeli kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Sindidzachita zimenezi chifukwa cha inuyo a nyumba ya Isiraeli, koma chifukwa cha dzina langa loyera limene munalidetsa pakati pa anthu a mitundu ina kumene munapita.”’+ 23 ‘Ndidzayeretsadi dzina langa lalikulu+ limene linadetsedwa pakati pa anthu a mitundu ina. Inu munadetsa dzina langalo pakati pa anthu a mitundu ina. Anthu a mitundu inawo adzadziwa kuti ine ndine Yehova,+ akadzaona zimene ndakuchitirani komanso adzadziwa kuti ndine Mulungu woyera,’ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. 24 ‘Ndidzakutengani kuchokera kwa anthu a mitundu ina nʼkukusonkhanitsani pamodzi kuchokera mʼmayiko onse ndipo ndidzakubwezeretsani mʼdziko lanu.+ 25 Ndidzakuwazani madzi oyera ndipo mudzakhala oyera.+ Ndidzakuyeretsani pokuchotserani zonyansa zanu zonse+ ndi mafano anu onse onyansa.+ 26 Ndidzakupatsani mtima watsopano+ ndipo ndidzaika mzimu watsopano mwa inu.+ Ndidzachotsa mtima wamwala+ mʼmatupi anu nʼkukupatsani mtima wamnofu.* 27 Ndidzaika mzimu wanga mwa inu ndipo ndidzachititsa kuti muziyenda motsatira malamulo anga.+ Mudzasunga zigamulo zanga komanso kuzitsatira. 28 Mukadzachita zimenezi mudzakhala mʼdziko limene ndinapatsa makolo anu. Mudzakhala anthu anga ndipo ine ndidzakhala Mulungu wanu.’+
29 ‘Ndidzakupulumutsani ku zinthu zanu zonse zodetsa ndipo ndidzauza mbewu kuti zibereke kwambiri moti sindidzakubweretseraninso njala.+ 30 Ndidzachititsa kuti zipatso za mtengo komanso zokolola zakumunda zichuluke nʼcholinga choti musadzanyozekenso chifukwa cha njala pakati pa anthu a mitundu ina.+ 31 Pa nthawiyo mudzakumbukira njira zanu zoipa ndi zochita zanu zimene sizinali zabwino. Mudzadzimvera chisoni chifukwa cha machimo anu komanso zinthu zonyansa zimene munkachita.+ 32 Koma dziwani izi: Ine sindikuchita zimenezi chifukwa cha inu,’+ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. ‘Koma inu a nyumba ya Isiraeli, muchite manyazi ndipo muone kuti mwanyozeka chifukwa cha njira zanu.’
33 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: ‘Pa tsiku limene ndidzakuyeretseni nʼkuchotsa zolakwa zanu zonse, ndidzachititsa kuti mʼmizinda yanu muzikhala anthu+ komanso kuti malo amene anali mabwinja amangidwenso.+ 34 Anthu adzalima mʼdziko limene linawonongedwa, limene aliyense wodutsa ankaliona kuti ndi bwinja. 35 Anthu adzanena kuti: “Dziko limene linali bwinja tsopano lakhala ngati munda wa Edeni.+ Mizinda imene inawonongedwa ija, imene inali mabwinja ndiponso imene nyumba zake zinagwetsedwa, tsopano ili ndi mipanda yolimba kwambiri ndipo mukukhala anthu.”+ 36 Anthu a mitundu ina amene anatsala omwe akuzungulirani, adzadziwa kuti ine Yehova, ndamanga zinthu zimene zinagwetsedwa komanso kuti ndadzala mitengo mʼdziko limene linali bwinja. Ine Yehova ndanena zimenezi ndipo ndazichita.’+
37 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: ‘Ine ndidzalolanso kuti a nyumba ya Isiraeli andipemphe kuti ndiwachulukitsire anthu awo ngati gulu la nkhosa ndipo ndidzachitadi zimenezo. 38 Mizinda imene inali mabwinja idzadzaza ndi anthu ochuluka+ ngati gulu la oyera ndiponso ngati nkhosa za ku Yerusalemu* pa nthawi ya zikondwerero,+ ndipo iwo adzadziwa kuti ine ndine Yehova.’”
37 Mphamvu za Yehova zinayamba kugwira ntchito pa ine* moti mzimu wa Yehova unanditenga nʼkukandikhazika pakati pa chigwa+ ndipo mʼchigwamo munali mafupa okhaokha. 2 Iye anandiyendetsa mʼchigwamo kuti ndione mafupa onsewo ndipo ndinaona kuti mʼchigwamo munali mafupa ambiri ndipo anali ouma kwambiri.+ 3 Ndiyeno anandifunsa kuti: “Iwe mwana wa munthu, kodi mafupawa angakhale ndi moyo?” Ine ndinayankha kuti: “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, inu ndi amene mukudziwa zimenezo.”+ 4 Ndiye anandiuza kuti: “Losera zokhudza mafupa amenewa ndipo uwauze kuti, ‘Inu mafupa ouma, imvani mawu a Yehova:
5 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wauza mafupa awa kuti: “Ndichititsa kuti mpweya ulowe mwa inu ndipo mukhala amoyo.+ 6 Ndidzakuikirani mitsempha komanso mnofu ndipo ndidzakukutirani ndi khungu nʼkuika mpweya mwa inu ndipo mudzakhala ndi moyo. Choncho mudzadziwa kuti ine ndine Yehova.”’”
7 Choncho ine ndinalosera mogwirizana ndi zimene anandilamula. Nditangolosera, panamveka phokoso la mafupa kuti gobedegobede! Ndipo mafupawo anayamba kubwera pamodzi nʼkumalumikizana. 8 Kenako ndinaona mitsempha ndi mnofu zikukuta mafupawo ndipo khungu linabwera pamwamba pake. Koma mʼmafupawo munalibe mpweya.
9 Kenako anandiuza kuti: “Losera kwa mphepo. Iwe mwana wa munthu, losera ndipo uuze mphepoyo kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Iwe mphepo,* bwera kuchokera kumbali zonse 4 nʼkuwomba anthu amene anaphedwawa kuti akhalenso ndi moyo.”’”
10 Choncho ndinalosera mogwirizana ndi zimene anandilamula ndipo mpweya* unalowa mwa iwo. Iwo anakhala ndi moyo ndipo anaimirira.+ Anali gulu lalikulu kwambiri la asilikali.
11 Kenako anandiuza kuti: “Iwe mwana wa munthu, mafupawa akuimira nyumba yonse ya Isiraeli.+ Iwo akunena kuti, ‘Mafupa athu auma ndipo tilibenso chiyembekezo chilichonse.+ Tatheratu!’ 12 Choncho losera, uwauze kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Ine ndidzatsegula manda anu,+ inu anthu anga ndipo ndidzakutulutsani mʼmandamo nʼkukubweretsani mʼdziko la Isiraeli.+ 13 Inu anthu anga, ine ndikadzatsegula manda anu nʼkukutulutsani mʼmandamo, mudzadziwa kuti ine ndine Yehova.”+ 14 Ndidzaika mzimu wanga mwa inu ndipo mudzakhala amoyo.+ Ndidzakukhazikani mʼdziko lanu ndipo mudzadziwa kuti ine Yehova ndinanena zimenezi ndipo ndazichita,’ akutero Yehova.”
15 Yehova anandiuzanso kuti: 16 “Koma iwe mwana wa munthu, tenga ndodo nʼkulembapo kuti, ‘Ndodo ya Yuda ndi Aisiraeli amene ali naye.’*+ Kenako utengenso ndodo ina nʼkulembapo kuti, ‘Ndodo ya Yosefe yoimira Efuraimu ndi onse amʼnyumba ya Isiraeli amene ali naye.’*+ 17 Ndiyeno uziike pamodzi kuti zikhale ndodo imodzi mʼdzanja lako.+ 18 Anthu a mtundu wako* akakufunsa kuti, ‘Kodi sutiuza kuti zinthu zimenezi zikutanthauza chiyani?’ 19 Uwauze kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Ine nditenga ndodo ya Yosefe ndi mafuko a Isiraeli amene ali naye. Ndodo imeneyi ili mʼdzanja la Efuraimu. Ndidzaiphatikiza ndi ndodo ya Yuda ndipo idzakhala ndodo imodzi.+ Iwo adzakhala ndodo imodzi mʼdzanja langa.”’ 20 Ndodo zimene wazilembazo zikhale mʼdzanja lako kuti azione.
21 Ndiye uwauze kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Ine nditenga Aisiraeli kuchokera kwa anthu a mitundu ina kumene anapita. Ndidzawasonkhanitsa pamodzi kuchokera kumbali zonse ndipo ndidzawabweretsa mʼdziko lawo.+ 22 Ndidzawachititsa kuti akhale mtundu umodzi mʼdzikolo+ ndipo azidzakhala mʼmapiri a Isiraeli. Onse azidzalamulidwa ndi mfumu imodzi+ ndipo sadzakhalanso mitundu iwiri kapena kugawanika nʼkukhala maufumu awiri.+ 23 Iwo sadzadziipitsanso ndi mafano awo onyansa,* zochita zawo zonyansa ndi zolakwa zawo zonse.+ Ndidzawapulumutsa ku zochita zawo zosakhulupirika zimene zinachititsa kuti achimwe ndipo ndidzawayeretsa. Iwo adzakhala anthu anga ndipo ine ndidzakhala Mulungu wawo.+
24 Mtumiki wanga Davide adzakhala mfumu yawo+ ndipo onsewo adzakhala ndi mʼbusa mmodzi.+ Iwo adzayenda motsatira zigamulo zanga ndiponso kusunga malamulo anga mosamala kwambiri.+ 25 Anthu amenewa adzakhala mʼdziko limene ndinapatsa mtumiki wanga Yakobo, dziko limene makolo anu ankakhala.+ Iwo adzakhala mʼdzikomo ndi ana awo* komanso zidzukulu zawo+ mpaka kalekale.+ Davide mtumiki wanga adzakhala mtsogoleri* wawo mpaka kalekale.+
26 Ndidzachita nawo pangano lamtendere+ ndipo pangano limeneli lidzakhalapo mpaka kalekale. Ine ndidzachititsa kuti akhazikike mʼdzikolo ndipo ndidzawachulukitsa+ komanso ndidzaika malo anga opatulika pakati pawo mpaka kalekale. 27 Tenti yanga idzakhala* pakati pawo.* Ine ndidzakhala Mulungu wawo ndipo iwo adzakhala anthu anga.+ 28 Malo anga opatulika akadzakhala pakati pawo mpaka kalekale, anthu a mitundu ina adzadziwa kuti ine Yehova, ndikuyeretsa Isiraeli.”’”+
38 Yehova anandiuzanso kuti: 2 “Iwe mwana wa munthu, yangʼana Gogi wa kudziko la Magogi,+ mtsogoleri wamkulu* wa Meseki ndi Tubala+ ndipo ulosere zoipa zimene zidzamuchitikire.+ 3 Unene kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Ine ndikupatsa chilango iwe Gogi, mtsogoleri wamkulu* wa Meseki ndi Tubala. 4 Ine ndidzakubweza nʼkukukola chibwano ndi ngowe.+ Kenako ndidzakupititsa kunkhondo limodzi ndi asilikali ako onse,+ mahatchi ako ndi amuna okwera pamahatchi ndipo onsewo adzavala mwaulemerero. Iwo adzakhala gulu lalikulu lonyamula zishango zazikulu ndi zazingʼono, ndipo onsewo ndi aluso lomenya nkhondo pogwiritsa ntchito malupanga. 5 Udzabwera limodzi ndi asilikali a ku Perisiya, Itiyopiya ndi Puti.+ Onsewa adzanyamula zishango zazingʼono ndipo adzavala zipewa. 6 Udzabweranso ndi Gomeri ndi magulu ake onse a asilikali, komanso ana a Togarima+ ochokera kumadera akutali kwambiri akumpoto. Iwo adzabwera ndi magulu awo onse a asilikali. Choncho iwe udzabwera ndi mitundu yambiri ya anthu.+
7 Khala wokonzeka, konzekera kumenya nkhondo, iweyo limodzi ndi asilikali ako onse amene asonkhana ndi iwe. Iweyo ukhala mtsogoleri* wawo.
8 Pakapita masiku ambiri, iwe udzaitanidwa. Ndiye pakadzapita zaka zambiri, udzalowa mʼdziko la anthu amene anabwerera kwawo. Anthu amenewa anapulumuka, lupanga litawononga dziko lawo. Kenako anasonkhanitsidwa pamodzi kuchokera kumitundu ina ya anthu nʼkukakhala kumapiri a ku Isiraeli amene anakhala ali owonongeka kwa nthawi yaitali. Anthu amene akukhala mʼdzikoli anawabwezeretsa kwawo kuchokera kwa anthu a mitundu ina. Onsewo akukhala mʼdzikoli motetezeka.+ 9 Iwe udzabwera mʼdzikolo ngati mphepo yamkuntho kudzawaukira. Iweyo, magulu a asilikali ako onse, pamodzi ndi anthu ambiri a mitundu ina, mudzaphimba dzikolo ngati mitambo.”’
10 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: ‘Pa tsiku limenelo, maganizo adzakubwerera mumtima mwako ndipo udzakonza chiwembu choipa kwambiri. 11 Udzanena kuti: “Ndikalowa mʼdziko limene midzi yake ndi yosatetezeka.+ Ndikaukira anthu amene akukhala mwabata, popanda chowasokoneza. Ndikaukira anthu onsewo amene akukhala mʼmidzi yopanda mipanda ndipo alibe zotsekera ndiponso mageti.” 12 Udzapita kumeneko kuti ukalande komanso kutengako zinthu zambiri, ndiponso kuti ukaukire malo owonongedwa amene tsopano mukukhala anthu.+ Udzapita kukaukira anthu amene anasonkhanitsidwanso pamodzi kuchokera kumitundu ina,+ amene akusonkhanitsa chuma ndi katundu,+ komanso amene akukhala pakatikati pa dziko lapansi.
13 Sheba+ ndi Dedani,+ amalonda a ku Tarisi+ ndi asilikali ake onse* adzakufunsa kuti: “Kodi walowa mʼdzikoli kuti ukalande zinthu zambiri? Kodi wasonkhanitsa asilikali ako kuti ukatenge siliva, golide, chuma ndi katundu? Kodi ukufuna ukalande zinthu zambiri zamʼdzikoli?”’
14 Choncho losera, iwe mwana wa munthu, ndipo uuze Gogi kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Pa tsiku limenelo, anthu anga Aisiraeli akamadzakhala mwabata, ndithu iwe udzadziwa zimenezo.+ 15 Udzabwera kuchokera kumalo ako, kumadera akutali kwambiri akumpoto.+ Udzabwera ndi mitundu yambiri ya anthu. Anthuwo adzakhala gulu lalikulu, adzakhala chigulu chachikulu cha asilikali. Onsewo adzabwera atakwera pamahatchi.+ 16 Mofanana ndi mitambo imene yaphimba dziko, iwe udzabwera kudzaukira anthu anga Aisiraeli. Mʼmasiku otsiriza, ine ndidzakubweretsa kuti uukire dziko langa+ nʼcholinga choti anthu a mitundu ina adzandidziwe ndikamadzadziyeretsa pamaso pawo, kudzera mwa iwe Gogi.”’+
17 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: ‘Kodi kale lija sindinkanena zokhudza iwe kudzera mwa atumiki anga, aneneri a Isiraeli? Aneneriwo analosera kwa zaka zambiri kuti ndidzakutumiza kwa iwo kuti ukawaukire.’
18 ‘Pa tsiku limenelo, tsiku limene Gogi adzalowe mʼdziko la Isiraeli, ndidzakhala ndi mkwiyo waukulu,’+ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. 19 ‘Ine ndidzalankhula mwaukali wanga woyaka moto komanso nditakwiya kwambiri. Ndipo pa tsiku limenelo mʼdziko la Isiraeli mudzachitika chivomerezi chachikulu. 20 Chifukwa cha ine, nsomba zamʼnyanja, mbalame zamumlengalenga, zilombo zakutchire, nyama zonse zimene zimakwawa panthaka ndiponso anthu onse apadziko lapansi, zidzanjenjemera. Mapiri adzagwa,+ malo otsetsereka adzagumuka ndipo khoma lililonse lidzagwera pansi.’
21 ‘Ndidzamuyambitsira nkhondo mʼmapiri anga onse kuti amuwononge,’ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. ‘Aliyense adzapha mʼbale wake ndi lupanga.+ 22 Ine ndidzamuweruza pomubweretsera mliri+ ndipo anthu ambiri adzafa. Ndidzamugwetsera mvula yamphamvu, matalala,+ moto+ ndi sulufule.+ Ndidzagwetsa zinthu zimenezi pa iyeyo, magulu a asilikali ake ndi mitundu yambiri ya anthu amene adzakhale kumbali yake.+ 23 Ndithu ndidzasonyeza mphamvu zanga, komanso ndidzasonyeza kuti ndine Mulungu woyera ndipo ndidzachititsa kuti anthu ambiri a mitundu ina andidziwe. Iwo adzadziwa kuti ine ndine Yehova.’”
39 “Iwe mwana wa munthu, losera zoipa zimene zidzachitikire Gogi+ ndipo umuuze kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Ine ndikupatsa chilango iwe Gogi, mtsogoleri wamkulu* wa Meseki ndi Tubala.+ 2 Ndidzakubweza nʼkukutsogolera kuti uchoke kumadera akutali kwambiri akumpoto+ ndipo ndidzakubweretsa kumapiri a ku Isiraeli. 3 Ndidzakuphumitsa uta mʼdzanja lako lamanzere ndipo ndidzachititsa kuti mivi yako igwe pansi kuchoka mʼdzanja lako lamanja. 4 Iwe udzafera mʼmapiri a ku Isiraeli+ limodzi ndi magulu ako onse a asilikali ndi anthu a mitundu ina amene adzakhale nawe. Ndidzakuperekani kwa mbalame zamitundumitundu zodya nyama ndi zilombo zakutchire kuti mukhale chakudya chawo.”’+
5 ‘Iweyo udzafera pamtetete,+ chifukwa ine ndanena zimenezi,’ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.
6 ‘Ndidzatumiza moto kuti ukawononge Magogi komanso anthu amene akukhala motetezeka mʼzilumba,+ ndipo anthu adzadziwa kuti ine ndine Yehova. 7 Ndidzachititsa kuti dzina langa loyera lidziwike pakati pa anthu anga Aisiraeli. Sindidzalolanso kuti dzina langa loyera lidetsedwe, ndipo anthu a mitundu ina adzadziwa kuti ine ndine Yehova,+ Mulungu Woyera mu Isiraeli.’+
8 ‘Inde, zimene ulosiwu ukunena zidzachitika ndipo zidzakwaniritsidwa,’ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. ‘Tsiku limene ndakhala ndikunena lija ndi limeneli. 9 Anthu amene akukhala mʼmizinda ya Isiraeli adzapita kukakoleza moto pogwiritsa ntchito zida zankhondo. Zida zake ndi zishango zazingʼono ndi zishango zazikulu, mauta ndi mivi, zibonga* ndi mikondo ingʼonoingʼono. Iwo adzagwiritsa ntchito zida zimenezi kwa zaka 7 pokoleza moto.+ 10 Iwo sadzafunika kunyamula mitengo kutchire kapena kutola nkhuni kunkhalango chifukwa chakuti adzagwiritsa ntchito zida zankhondozo pokoleza moto.’
‘Adzalanda zinthu za anthu amene anawalanda zinthu zawo ndipo adzatenga katundu wa anthu amene anatenga katundu wawo,’ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.
11 ‘Pa tsiku limenelo Gogi+ ndidzamupatsa malo kuti akhale manda ake ku Isiraeli komweko, mʼchigwa chimene anthu amene amapita kumʼmawa kwa nyanja amadutsa, ndipo chigwacho chidzatseka njira imene anthu amadutsa. Kumeneko nʼkumene adzaike mʼmanda Gogi limodzi ndi magulu onse a anthu amene ankamutsatira ndipo adzalitchula kuti Chigwa cha Hamoni-Gogi.*+ 12 A nyumba ya Isiraeli adzatenga miyezi 7 akuika mʼmanda Gogi ndi gulu lake kuti ayeretse dzikolo.+ 13 Anthu onse amʼdzikolo adzagwira ntchito yoika mʼmanda anthuwo. Iwo adzatchuka chifukwa cha ntchito imeneyi pa tsiku limene ine ndidzalemekezeke,’+ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.
14 ‘Anthu adzapatsidwa ntchito yoti azidzazungulira mʼdzikomo nthawi zonse nʼkumakwirira mitembo imene yatsala pamtunda kuti ayeretse dziko. Iwo adzakhala akufunafuna mitembo kwa miyezi 7. 15 Anthu amene akungodutsa mʼdzikolo akaona fupa la munthu, azidzaika chizindikiro pafupi ndi fupalo. Kenako anthu amene anapatsidwa ntchito yokwirira mitembo aja adzalikwirira mʼChigwa cha Hamoni-Gogi.+ 16 Kumeneko kudzakhalanso mzinda wotchedwa Hamona.* Ndipo anthu adzayeretsa dzikolo.’+
17 Koma iwe mwana wa munthu, Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: ‘Uza mbalame zamtundu uliwonse ndi zilombo zonse zakutchire kuti, “Sonkhanani pamodzi ndipo mubwere kuno. Zungulirani nsembe yanga imene ndikukukonzerani. Imeneyi ndi nsembe yaikulu mʼmapiri a ku Isiraeli.+ Mukabwera mudzadya nyama ndi kumwa magazi.+ 18 Mudzadya mnofu wa anthu amphamvu komanso kumwa magazi a atsogoleri a dziko lapansi, omwe ndi nkhosa zamphongo, ana a nkhosa amphongo, mbuzi ndi ngʼombe zamphongo, nyama zonse zonenepa za ku Basana. 19 Inu mudzadya mafuta mosusuka ndipo mudzamwa magazi mpaka mutaledzera ndi nsembe imene ndidzakukonzereni.”’
20 ‘Patebulo langa mudzadya nʼkukhuta nyama ya mahatchi, ya okwera magaleta, ya anthu amphamvu ndi asilikali osiyanasiyana,’+ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.
21 ‘Ndidzasonyeza ulemerero wanga pakati pa anthu a mitundu ina ndipo mitundu yonse ya anthu idzaona chiweruzo chimene ndapereka komanso mphamvu zimene* ndasonyeza pakati pawo.+ 22 Kuyambira tsiku limenelo mpaka mʼtsogolo, a nyumba ya Isiraeli adzadziwa kuti ine ndine Yehova, Mulungu wawo. 23 Anthu a mitundu ina adzadziwa kuti a nyumba ya Isiraeli anatengedwa kupita ku ukapolo chifukwa cha zolakwa zawo, popeza anandichitira zinthu mosakhulupirika.+ Choncho ine ndinawabisira nkhope yanga+ nʼkuwapereka kwa adani awo+ ndipo onse anaphedwa ndi lupanga. 24 Ndinawachitira zinthu mogwirizana ndi zonyansa zimene anachita komanso chifukwa chakuti anaphwanya malamulo, moti ndinawabisira nkhope yanga.’
25 Choncho Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: ‘Ndidzabwezeretsa ana a Yakobo+ omwe anatengedwa kupita kumayiko ena ndipo ndidzachitira chifundo nyumba yonse ya Isiraeli.+ Ndi mphamvu zanga zonse, ndidzateteza dzina langa loyera.*+ 26 Akadzachititsidwa manyazi chifukwa cha zinthu zonse zosakhulupirika zimene anandichitira,+ adzakhala mʼdziko lawo motetezeka, popanda wowaopseza.+ 27 Ndikadzawabweretsa kuchokera kumitundu ina ya anthu ndi kuwasonkhanitsa pamodzi kuchokera kumayiko a adani awo,+ ndidzadziyeretsa pakati pawo pamaso pa mitundu yambiri ya anthu.’+
28 ‘Iwo adzadziwa kuti ine ndine Yehova Mulungu wawo, ndikadzawapititsa ku ukapolo pakati pa anthu a mitundu ina, kenako nʼkuwabwezeretsa kudziko lawo osasiyako wina aliyense.+ 29 Sindidzawabisiranso nkhope yanga+ chifukwa panyumba ya Isiraeli ndidzatsanulirapo mzimu wanga,’+ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”
40 Mʼchaka cha 25 kuchokera pamene tinatengedwa kupita ku ukapolo,+ kuchiyambi kwa chakacho, pa tsiku la 10 la mwezi woyamba, mʼchaka cha 14 pambuyo poti mzinda wawonongedwa,+ pa tsiku limeneli mphamvu za Yehova zinayamba kugwira ntchito pa ine,* ndipo iye ananditenga nʼkupita nane kumzinda.+ 2 Kudzera mʼmasomphenya ochokera kwa Mulungu, iye ananditenga nʼkupita nane mʼdziko la Isiraeli nʼkukandikhazika paphiri lalitali kwambiri.+ Mbali yakumʼmwera paphiripo panali chinachake chooneka ngati mzinda.
3 Atafika nane kumeneko, ndinaona munthu wamwamuna amene maonekedwe ake anali ofanana ndi kopa.*+ Mʼmanja mwake munali chingwe cha fulakesi* ndi bango loyezera*+ ndipo anaima pakhomo lapageti. 4 Munthuyo anandiuza kuti: “Iwe mwana wa munthu, uonetsetse, umvetsere mwatcheru ndipo uchite chidwi ndi zonse* zimene ndikuonetse, chifukwa ndakubweretsa kuno kuti udzachite zimenezi. Ukauze nyumba ya Isiraeli zonse zimene uone.”+
5 Ndiyeno ndinaona mpanda umene unazungulira kachisi.* Mʼmanja mwa munthu uja munali bango loyezera lokwana mikono 6 kutalika kwake (pa mkono uliwonse anawonjezerapo chikhatho chimodzi).* Iye anayamba kuyeza mpandawo ndipo anapeza kuti unali wochindikala bango limodzi komanso kuchoka pansi kupita mʼmwamba unali wautali bango limodzi.
6 Kenako anafika pageti limene linayangʼana kumʼmawa+ nʼkukwera masitepe ake. Atayeza malo apafupi ndi khomo la kanyumba kapagetiko, anapeza kuti anali bango limodzi mulifupi. Malo apafupi ndi khomo lambali ina ya kanyumbako analinso bango limodzi mulifupi mwake. 7 Chipinda cha alonda chilichonse chinali bango limodzi mulitali ndi bango limodzi mulifupi. Kuchoka pachipinda chimodzi kukafika pachipinda china panali mikono 5.+ Malo apafupi ndi khomo la kanyumbako, pafupi ndi khonde limene linayangʼanizana ndi kachisi, anali bango limodzi.
8 Munthu uja anayeza khonde la kanyumbako loyangʼana bwalo lakunja, ndipo anapeza kuti linali bango limodzi. 9 Kenako anayeza khonde la kanyumba kapageti nʼkupeza kuti linali mikono 8. Anayezanso zipilala zake zamʼmbali, nʼkupeza kuti zinali mikono iwiri. Khonde la kanyumbako linali kumbali imene inayangʼanizana ndi kachisi.
10 Kumbali iliyonse ya geti lakumʼmawa kunali zipinda zitatu za alonda. Zipinda zitatuzo zinali zazikulu mofanana, ndipo zipilala zamʼmbali zimene zinali mbali iliyonse zinalinso zofanana.
11 Kenako anayeza mulifupi mwa malo apafupi ndi khomo la kanyumba kapageti nʼkupeza mikono 10. Mulitali mwa getilo munali mikono 13.
12 Malo otchinga ndi mpanda, kutsogolo kwa zipinda za alonda, anali mkono umodzi mbali zonse. Chipinda cha alonda chilichonse pa kanyumbako, chinali mikono 6.
13 Kenako anayeza kanyumba kapagetiko kuchokera padenga la chipinda chimodzi cha alonda* kukafika padenga la chipinda china ndipo anapeza mikono 25. Khomo lililonse la chipinda cha alonda linali moyangʼanizana ndi khomo la chipinda cha mbali inayo.+ 14 Kenako anayeza zipilala zamʼmbali ndipo anapeza kuti zinali zazitali mikono 60. Zinalinso chimodzimodzi ndi zipilala zamʼmbali zimene zinali mʼmageti a mbali zina za bwaloli. 15 Kuchokera kutsogolo kwa khomo lakunja la kanyumba kapageti, kukafika kutsogolo kwa khonde, kumbali imene yayangʼanizana ndi kachisi, panali mikono 50.
16 Zipinda za alondazo komanso zipilala zimene zinali mʼmbali mwa zipindazo zinali ndi mawindo amene anali ndi mafelemu aakulu mkati koma aangʼono kunja+ kuzungulira kanyumba konseko. Mkati mwa makonde munalinso mawindo mbali zonse ndipo pazipilala zamʼmbali panali zithunzi za mtengo wa kanjedza.+
17 Kenako anandipititsa mʼbwalo lakunja. Kumeneko ndinaona zipinda zodyera*+ ndipo pansi pa bwalo lonselo panali powaka. Pabwalo lowakalo panali zipinda zodyera zokwana 30. 18 Mulifupi mwa malo owaka miyala amʼmbali mwa tinyumba tapageti munali mofanana ndi mulitali mwa tinyumbato. Malo owaka amenewa anali otsika poyerekezera ndi bwalo lamkati.
19 Kenako munthu uja anayeza mtunda* wochokera kutsogolo kwa kanyumba kapageti lamʼmunsi kukafika pamene panayambira bwalo lamkati. Malo amenewa anali mikono 100, kumʼmawa ndi kumpoto.
20 Bwalo lakunja linali ndi kanyumba kapageti kamene kanayangʼana kumpoto. Iye anayeza mulitali ndi mulifupi mwake. 21 Kanyumba kapagetiko kanali ndi zipinda zitatu za alonda mbali iliyonse. Miyezo ya zipilala zake zamʼmbali komanso khonde lake, inali yofanana ndi ya kanyumba kapageti koyamba kaja. Kanyumbako kanali mikono 50 mulitali ndi mikono 25 mulifupi. 22 Miyezo ya mawindo ake, khonde lake ndi zithunzi zake za mtengo wa kanjedza,+ inali yofanana ndi zimene zinali pakanyumba kapageti kakumʼmawa. Anthu akafuna kulowa mʼkanyumbako amakwera masitepe 7 ndipo khonde lake linali kutsogolo kwa masitepewo.
23 Mʼbwalo lamkati munali geti limene linayangʼanizana ndi geti lakumpoto ndipo geti lina linayangʼanizana ndi geti lakumʼmawa. Munthu uja anayeza mtunda wochokera pageti limodzi kukafika pageti lina ndipo anapeza kuti unali mikono 100.
24 Kenako ananditengera kumbali yakumʼmwera ndipo ndinaona kuti kumeneko kuli kanyumba kapageti kamene kanayangʼana kumʼmwera.+ Iye anayeza zipilala zake zamʼmbali ndi khonde lake ndipo miyezo yake inali yofanana ndi ya tinyumba tina tija. 25 Kumbali iliyonse ya kanyumba kameneka komanso khonde lake kunali mawindo ofanana ndi a tinyumba tina tija. Kanyumbako kanali mikono 50 mulitali ndi mikono 25 mulifupi. 26 Munthu akafuna kulowa mʼkanyumbako amakwera masitepe 7+ ndipo khonde lake linali kutsogolo kwa masitepewo. Kumbali iliyonse ya khondelo kunali chipilala chimodzi ndipo pazipilalazo panali zithunzi za mtengo wa kanjedza.
27 Bwalo lamkati linali ndi geti limene linayangʼana kumʼmwera. Iye anayeza kuchokera pagetipo kulowera kumʼmwera kukafika pageti lina ndipo anapeza kuti panali mtunda wokwana mikono 100. 28 Kenako anandipititsa mʼbwalo lamkati kudzera pageti lakumʼmwera. Atayeza kanyumba kapageti kakumʼmwera anapeza kuti miyezo yake inali yofanana ndi tinyumba tina tija. 29 Miyezo ya zipinda za alonda za kanyumba kapagetiko, zipilala zake zamʼmbali ndi khonde lake inali yofanana ndi ya tinyumba tina tija. Kumbali iliyonse ya kanyumbako komanso khonde lake kunali mawindo. Kanyumbako kanali mikono 50 mulitali ndi mikono 25 mulifupi.+ 30 Tinyumba tonse tapageti tinali ndi khonde. Khonde lililonse linali mikono 25 mulitali ndi mikono 5 mulifupi. 31 Khonde lake linayangʼana kubwalo lakunja ndipo pazipilala zake zamʼmbali panali zithunzi za mtengo wa kanjedza+ ndipo anthu akafuna kulowa mʼkanyumbako amakwera masitepe 8.+
32 Atandilowetsa mʼbwalo lamkati kudzera kumʼmawa, anayeza kanyumba kapagetiko ndipo anapeza kuti miyezo yake ndi yofanana ndi ya tinyumba tina tija. 33 Miyezo ya zipinda za alonda za kanyumba kapagetiko, zipilala zake zamʼmbali ndi khonde lake inali yofanana ndi miyezo ya tinyumba tina tija. Kumbali iliyonse ya kanyumbako komanso khonde lake kunali mawindo. Kanyumbako kanali mikono 50 mulitali ndi mikono 25 mulifupi. 34 Khonde lake linayangʼana kubwalo lakunja ndipo pazipilala zake zamʼmbali panali zithunzi za mtengo wa kanjedza ndipo anthu akafuna kulowa mʼkanyumbako amakwera masitepe 8.
35 Kenako anandipititsa kugeti la kumpoto.+ Atayeza kanyumba kapagetiko, anapeza kuti miyezo yake inali yofanana ndi ya tinyumba tina tija. 36 Miyezo ya zipinda za alonda za kanyumba kapagetiko, zipilala zake zamʼmbali ndi khonde lake inali yofanana ndi miyezo ya tinyumba tina tija. Kumbali iliyonse ya kanyumbako komanso khonde lake kunali mawindo. Kanyumbako kanali mikono 50 mulitali ndi mikono 25 mulifupi. 37 Zipilala zake zamʼmbali zinayangʼana kubwalo lakunja ndipo pazipilala zonsezo panali zithunzi za mtengo wa kanjedza. Anthu akafuna kulowa mʼkanyumbako amakwera masitepe 8.
38 Pafupi ndi zipilala zamʼmbali mwa tinyumba tapagetito panali chipinda chodyera komanso khomo lake, kumene ankatsukira nsembe zopsereza zathunthu.+
39 Kumbali iliyonse ya khonde la kanyumba kapagetiko kunali matebulo awiri, pamene ankapherapo nsembe zopsereza zathunthu,+ nsembe zamachimo+ ndi nsembe zakupalamula.+ 40 Panja pa khomo lolowera mʼkanyumba kambali ya kumpoto panali matebulo awiri. Kumbali ina ya khonde la kanyumbako, kunalinso matebulo ena awiri. 41 Kumbali iliyonse ya kanyumba kapageti kunali matebulo 4 ndipo mkati mwa kanyumbako munalinso matebulo 4. Matebulo onse amene ankapherapo nyama zoti apereke nsembe analipo 8. 42 Matebulo 4 a nsembe zopsereza zathunthuwo anali amiyala yosema. Mulitali mwake anali mkono umodzi ndi hafu, mulifupi mwake anali mkono umodzi ndi hafu ndipo kuchoka pansi kufika pamwamba anali mkono umodzi. Pamatebulo amenewa ankaikapo zida zophera nyama ya nsembe zopsereza zathunthu ndi nsembe zina. 43 Kuzungulira khoma lonse lamkati anaikamo mashelefu amene anali chikhatho chimodzi mulifupi. Nyama za nsembe zimene ankapereka ngati mphatso ankaziika pamatebulo aja.
44 Kunja kwa kanyumba kapageti kamkati kunali zipinda zodyeramo oimba.+ Zipindazi zinali mʼbwalo lamkati pafupi ndi geti lakumpoto ndipo zinayangʼana kumʼmwera. Chipinda china chinali pafupi ndi geti lakumʼmawa ndipo chinayangʼana kumpoto.
45 Munthu uja anandiuza kuti: “Chipinda chodyeramo ichi, chimene chayangʼana kumʼmwera, ndi cha ansembe amene amagwira ntchito zokhudza utumiki wapakachisi.+ 46 Chipinda chodyeramo chimene chayangʼana kumpoto ndi cha ansembe amene amagwira ntchito zokhudza utumiki wapaguwa lansembe,+ omwe ndi ana a Zadoki.+ Amenewa ndi Alevi amene anapatsidwa udindo woti azifika pamaso pa Yehova nʼkumamutumikira.”+
47 Kenako munthu uja anayeza bwalo lamkati. Iye anapeza kuti mulitali linali mikono 100 ndipo mulifupi linalinso mikono 100. Bwalolo linali lofanana mbali zonse 4. Guwa lansembe linali kutsogolo kwa kachisi.
48 Kenako anandipititsa pakhonde la kachisi+ ndipo anayeza chipilala chamʼmbali cha khondelo nʼkupeza kuti chinali mikono 5 mbali imodzi komanso mikono 5 mbali inayo. Mulifupi mwa geti la kachisiyo munali mikono itatu mbali imodzi komanso mikono itatu mbali inayo.
49 Khondelo linali mikono 20 mulitali ndi mikono 11* mulifupi. Kuti anthu afike pakhondepo ankakwera masitepe. Pafupi ndi zipilala zamʼmbalizo panali nsanamira, imodzi mbali iyi, ina mbali inayo.+
41 Kenako munthu uja anandipititsa mʼmalo oyera,* ndipo anayeza zipilala zamʼmbali. Chipilala cha mbali imodzi chinali mikono* 6 mulifupi ndipo cha mbali ina chinalinso mikono 6 mulifupi. 2 Khomo lolowera linali mikono 10 mulifupi, ndipo makoma apakhomopo anali* mikono 5 mbali imodzi, ndi mikono 5 mbali inayo. Anayeza chipinda chakunja ndipo anapeza kuti chinali mikono 40 mulitali, mulifupi chinali mikono 20.
3 Kenako analowa mʼchipinda chamkati* nʼkuyeza chipilala chamʼmbali chapakhomo ndipo anapeza kuti kuchindikala kwake chinali mikono iwiri. Anapezanso kuti khomo linali mikono 6 ndipo makoma a khomolo anali* mikono 7. 4 Kenako anayeza chipinda chimene chinayangʼanizana ndi malo oyera, ndipo anapeza kuti chinali mikono 20 mulitali ndi mikono 20 mulifupi.+ Ndiyeno anandiuza kuti: “Amenewa ndi Malo Oyera Koposa.”+
5 Kenako anayeza khoma la kachisi ndipo anapeza kuti kuchindikala kwake linali mikono 6. Zipinda zamʼmbali kuzungulira kachisi yenseyo zinali mikono 4 mulifupi.+ 6 Zipinda zamʼmbalizo zinali zosanjikizana katatu ndipo nsanjika iliyonse inali ndi zipinda 30. Kuzungulira khoma la kachisiyo panali timakonde timene tinali ngati maziko a zipinda zamʼmbali moti khoma la zipindazo linaima bwinobwino popanda kubowola khoma la kachisi.+ 7 Mʼmbali zonse za kachisiyo munali masitepe oyenda chozungulira opitira mʼzipinda zamʼmwamba amene ankakulirakulira akamakwera mʼmwamba.+ Zipinda za nsanjika yachitatu zinali zokulirapo kuposa za nsanjika yachiwiri, ndipo zipinda za nsanjika yachiwiri zinali zokulirapo kuposa za nyumba yapansi. Munthu akafuna kupita kuzipinda zamʼmwamba kuchokera kuzipinda zapansi ankadutsa mʼzipinda zapakati.
8 Ndinaona kuti kachisi yenseyo anamumanga pamaziko okwera. Maziko a zipinda zamʼmbali anali bango lathunthu, yomwe ndi mikono 6, kuchokera pansi kukafika polumikizira. 9 Khoma lakunja la zipinda zamʼmbali linali lochindikala mikono 5. Panali mpata* kuchokera mʼmphepete mwa maziko kukafika pamene panayambira khoma la zipinda zamʼmbali zimene zinali mbali ya kachisi.
10 Kuchokera pakachisi kukafika kuzipinda zodyera+ panali malo omwe anali mikono 20 mulifupi, kumbali zonse. 11 Pakati pa zipinda zamʼmbali ndi mpata umene unali mbali yakumpoto panali khomo ndipo khomo lina linali mbali yakumʼmwera. Mpatawo unali mikono 5 mulifupi, kuzungulira mbali zonse.
12 Kumadzulo kwa kachisi kunalinso nyumba ina imene inayangʼanizana ndi malo opanda kanthu. Nyumbayi inali mikono 70 mulifupi ndipo mulitali mwake inali mikono 90. Khoma la nyumbayo linali lochindikala mikono 5, kuzungulira nyumba yonseyo.
13 Munthu uja anayeza kachisi nʼkupeza kuti anali mikono 100 mulitali. Ndipo malo opanda kanthu aja, nyumba ija* ndi makoma ake zinalinso mikono 100 mulitali. 14 Mbali yakutsogolo kwa kachisi yomwe inayangʼana kumʼmawa limodzi ndi malo opanda kanthu aja zinali mikono 100 mulifupi.
15 Munthu uja anayeza kumbuyo kwa nyumba yomwe inayangʼanizana ndi malo opanda kanthu aja limodzi ndi timakonde take kumbali zonse ndipo anapeza kuti zinali mikono 100 mulitali.
Anayezanso Malo Oyera ndi Malo Oyera Koposa+ komanso makonde a bwalo, 16 malo apafupi ndi khomo, mawindo a mafelemu aakulu mkati koma aangʼono kunja+ ndiponso timakonde timene tinali mʼmalo atatuwo. Pafupi ndi malo apakhomowo anakhomapo matabwa+ kuchokera pansi kufika mʼmawindo, ndipo mawindowo anali otchinga. 17 Anayeza pamwamba pa khomo, kunja ndi mkati mwa kachisi komanso kuzungulira khoma lonse la kachisiyo. 18 Kachisiyo anali ndi zithunzi zojambula mochita kugoba za akerubi+ ndi za mitengo ya kanjedza.+ Mtengo uliwonse wa kanjedza unali pakati pa akerubi awiri ndipo kerubi aliyense anali ndi nkhope ziwiri. 19 Nkhope ya munthu inayangʼana mtengo wa kanjedza kumbali imodzi ndipo nkhope ya mkango* inayangʼana mtengo wa kanjedza kumbali inayo.+ Zithunzizi zinajambulidwa mofanana kuzungulira kachisi yenseyo. 20 Pakhoma la kachisiyo, kuyambira pansi mpaka pamwamba pa khomo, anajambulapo mochita kugoba zithunzi za akerubi ndi za mitengo ya kanjedza.
21 Mafelemu apamakomo a kachisi anali ofanana mbali zonse.*+ Kutsogolo kwa malo oyera* kunali chinachake chooneka ngati 22 guwa lansembe lamatabwa+ limene linali mikono itatu kuchokera pansi kufika pamwamba ndipo mulitali mwake linali mikono iwiri. Guwalo linali ndi zochirikizira mʼmakona ndipo pansi pake* ndiponso mʼmbali mwake munali mwamatabwa. Ndiyeno munthu uja anandiuza kuti: “Ili ndi tebulo limene lili pamaso pa Yehova.”+
23 Khomo la Malo Oyera linali ndi zitseko ziwiri ndipo khomo la Malo Oyera Koposa linalinso ndi zitseko ziwiri.+ 24 Khomo lililonse linali ndi zitseko ziwiri zimene zinkatheka kuzitsegula. 25 Pazitseko za kachisi panali zithunzi zojambula mochita kugoba za akerubi ndi za mitengo ya kanjedza zofanana ndi zimene zinali mʼmakoma.+ Kutsogolo kwa denga la khonde anakhomako matabwa otulukira kunja. 26 Mʼmbali zonse za khoma lapakhonde komanso mʼzipinda zamʼmbali za kachisi ndi pamatabwawo, munali mawindo a mafelemu aakulu mkati koma aangʼono kunja,+ ndipo anajambulamo zithunzi za mtengo wa kanjedza.
42 Kenako munthu uja anandipititsa kubwalo lakunja mbali yakumpoto.+ Ndiyeno anandipititsa kunyumba imene inali ndi zipinda zodyera yomwe inali pafupi ndi malo opanda kanthu,+ kumpoto kwa nyumba imene inali kumadzulo.*+ 2 Mulitali mwa nyumbayo kumbali yakhomo lakumpoto, munali mikono 100* ndipo mulifupi mwake inali mikono 50. 3 Nyumbayi inali pakati pa bwalo lamkati lomwe linali mikono 20 mulifupi+ ndi malo owaka miyala amʼbwalo lakunja. Panali nyumba ziwiri zoyangʼanizana, zomwe zinali ndi zipinda zodyera. Nyumbazo zinali zosanjikizana katatu ndipo zinali ndi makonde omwe anali moyangʼanizana. 4 Pakati pa nyumbazo* panali njira+ imene inali mikono 10 mulifupi ndi mikono 100 mulitali* ndipo makomo olowera mʼnyumbazo anali mbali yakumpoto. 5 Zipinda zodyera zamʼmwamba zinali zocheperapo kusiyana ndi zapakati komanso zapansi chifukwa chakuti makonde anatenga malo ena a zipindazo. 6 Nyumbazo zinali zosanjikizana katatu koma zinalibe zipilala ngati zamʼmabwalo. Nʼchifukwa chake zipinda zamʼmwamba zinali zazingʼono kusiyana ndi zipinda zapakati komanso zapansi.
7 Mpanda wamiyala umene unali kunja, pafupi ndi zipinda zodyera unali mikono 50 mulitali mwake. Mpandawo unali mbali yakubwalo lakunja ndipo unayangʼanizana ndi zipinda zina zodyera. 8 Zipinda zodyera zimene zinali kumbali ya bwalo lakunja zinali mikono 50 mulitali, koma zimene zinali kumbali ya kachisi zinali mikono 100 mulitali mwake. 9 Kumʼmawa kwa nyumba yodyera, kunali khomo limene munthu ankatha kulowa akamachokera mʼbwalo lakunja.
10 Pafupi ndi malo opanda kanthu komanso nyumba imene inali kumadzulo, mkati* mwa mpanda wamiyala wa bwalo, kumbali yakumʼmawa, kunalinso nyumba zodyera.+ 11 Pakati pa nyumba zodyerazo panali njira yofanana ndi ya nyumba zodyera za mbali yakumpoto.+ Mulitali ndi mulifupi mwa nyumbazo, makomo otulukira komanso kamangidwe kake zinali zofanana ndi za nyumba za kumpoto zija. Makomo ake olowera 12 anali ofanana ndi makomo olowera a nyumba zimene zinali kumbali yakumʼmwera zija. Pamene panayambira njira panali khomo lolowera. Khomoli linali pafupi ndi mpanda wamiyala kumbali yakumʼmawa, pamene munthu ankatha kulowera.+
13 Ndiyeno munthu uja anandiuza kuti: “Nyumba zodyera zakumpoto ndi zakumʼmwera zimene zili pafupi ndi malo opanda kanthu,+ ndi nyumba zodyera zopatulika, kumene ansembe otumikira Yehova amadyerako nsembe zopatulika koposa.+ Mʼnyumbazo amaikamo nsembe zopatulika koposa zomwe ndi nsembe zambewu, nsembe zamachimo ndi nsembe zakupalamula, chifukwa malo amenewa ndi oyera.+ 14 Ansembe akalowa mʼnyumbazo asamatuluke mʼmalo oyerawo kupita kubwalo lakunja asanavule zovala zimene amavala potumikira,+ chifukwa zovala zimenezi nʼzopatulika. Akafuna kupita kumalo amene anthu ena onse amaloledwa kufikako, azivala zovala zina.”
15 Atamaliza kuyeza malo amkati a kachisi,* ananditulutsa kunja kudzera pageti limene linayangʼana kumʼmawa+ ndipo anayeza malo onsewo.
16 Iye anayeza mbali yakumʼmawa ndi bango loyezera.* Mogwirizana ndi bango loyezeralo, malo onsewo anakwana mabango 500.
17 Anayezanso mbali yakumpoto ndipo mogwirizana ndi bango loyezera, malowo anakwana mabango 500.
18 Anayezanso mbali yakumʼmwera ndipo mogwirizana ndi bango loyezera, malowo anakwana mabango 500.
19 Kenako anazungulira kupita mbali yakumadzulo. Kumeneko anayeza malowo ndi bango loyezera ndipo anakwana mabango 500.
20 Anayeza malowo mbali zonse 4. Malo onsewo anali ndi mpanda+ umene unali mabango 500 mulitali ndi mabango 500 mulifupi mwake.+ Mpandawo unkasiyanitsa malo opatulika ndi malo wamba.+
43 Kenako munthu uja anandipititsa kugeti limene linayangʼana kumʼmawa.+ 2 Kumeneko ndinaona ulemerero wa Mulungu wa Isiraeli ukubwera kuchokera kumʼmawa+ ndipo mawu ake ankamveka ngati mkokomo wa madzi.+ Dziko lapansi linawala chifukwa cha ulemerero wake.+ 3 Zimene ndinaonazo zinali zofanana ndi zimene ndinaona mʼmasomphenya ena pamene ndinapita* kukawononga mzinda. Ndinaona zinthu zofanana ndi zimene ndinaona mʼmphepete mwa mtsinje wa Kebara.+ Nditaona zimenezo, ndinagwada nʼkuwerama mpaka nkhope yanga pansi.
4 Ndiyeno ulemerero wa Yehova unalowa mʼkachisi* kudzera pageti limene linayangʼana kumʼmawa.+ 5 Kenako mzimu unandidzutsa mʼkupita nane mʼbwalo lamkati ndipo ndinaona kuti ulemerero wa Yehova wadzaza mʼkachisi muja.+ 6 Ndiyeno ndinamva wina akulankhula nane kuchokera mʼkachisi ndipo munthu uja anabwera nʼkudzaima pambali panga.+ 7 Iye anandiuza kuti:
“Iwe mwana wa munthu, awa ndi malo a mpando wanga wachifumu+ ndiponso poikapo mapazi anga.+ Ndidzakhala pamalo amenewa, pakati pa Aisiraeli mpaka kalekale.+ Nyumba ya Isiraeli ndi mafumu awo sadzaipitsanso dzina langa loyera+ pochita uhule ndi milungu ina komanso ndi mitembo ya mafumu awo. 8 Iwo anaipitsa dzina langa loyera chifukwa cha zinthu zonyansa zimene anachita pamene anaika khomo lawo pafupi ndi khomo langa, nʼkuika felemu la khomo lawo pafupi ndi felemu la khomo langa moti pakati pa iwowo ndi ine nʼkungokhala khoma lokha lotisiyanitsa.+ Choncho ndinawawononga nditakwiya.+ 9 Tsopano asiye kuchita zauhule ndi milungu ina ndipo achotse mitembo ya mafumu awo nʼkukaiika kutali ndi ine. Akatero ine ndidzakhala pakati pawo mpaka kalekale.+
10 Koma iwe mwana wa munthu, ufotokozere nyumba ya Isiraeli za kachisiyu+ kuti achite manyazi chifukwa cha zolakwa zawo,+ ndipo iwo aonetsetse pulani ya kachisiyu* kuti adziwe mmene anamangidwira. 11 Ngati atachita manyazi chifukwa cha zonse zimene anachita, uwauze za pulani ya kachisiyu, kamangidwe kake, makomo ake olowera ndi otulukira.+ Uwasonyeze pulani yake yonse komanso uwadziwitse malangizo ndi malamulo ake. Uwalembe iwo akuona nʼcholinga choti adziwe mbali zosiyanasiyana za kachisiyo nʼkumatsatira malamulo apakachisipo.+ 12 Ili ndi lamulo lokhudza kachisi. Malo onse apamwamba pa phiri ndi oyera koposa.+ Limeneli ndi lamulo lokhudza kachisi.
13 Iyi ndi miyezo ya guwa lansembe pogwiritsa ntchito muyezo wa mkono+ (pa mkono uliwonse anawonjezerapo chikhatho chimodzi).* Chigawo chapansi cha guwa lansembe nʼchachitali mkono umodzi ndipo mulifupi mwake ndi mkono umodzi. Guwali lili ndi mkombero wokwana chikhatho* chimodzi mulifupi ndipo wazungulira mʼmbali mwake. Chimenechi ndi chigawo chapansi cha guwa la nsembe. 14 Kuchokera pachigawo chapansi, chigawo chachiwiri cha guwa la nsembe nʼchachitali mikono iwiri ndipo mʼmbali mwake nʼchachikulu mkono umodzi kuposa chigawo chachitatu kumbali zonse. Chigawo chachitatu nʼchachitali mikono 4 ndipo mʼmbali mwake nʼchachikulu mkono umodzi kuposa malo osonkhapo moto kumbali zonse. 15 Malo osonkhapo moto ndi aatali mikono 4 ndipo mʼmakona mwa malo osonkhapo motowo muli nyanga 4.+ 16 Malo osonkhapo motowo ndi ofanana mbali zonse. Mulitali mwake ndi mikono 12 ndipo mulifupi mwake ndi mikononso 12.+ 17 Mbali zonse 4 za chigawo chachitatu ndi zokwana mikono 14 mulitali ndiponso mikono 14 mulifupi. Kakhoma kamʼmphepete mwake ndi kokwana hafu ya mkono, ndipo pansi pake ndi pokwana mkono umodzi kumbali zonse.
Masitepe a guwalo ali kumʼmawa.”
18 Ndiyeno munthu uja anandiuza kuti, “Iwe mwana wa munthu, Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa wanena kuti: ‘Amenewa ndi malangizo amene akuyenera kutsatiridwa popanga guwa lansembe kuti aziperekerapo nsembe zopsereza zathunthu ndi kuwazapo magazi.+
19 Ana a Zadoki, omwe ndi Alevi ansembe,+ amene amayandikira kwa ine nʼkumanditumikira, uwapatse ngʼombe yaingʼono yamphongo kuchokera pagulu la ziweto kuti ikhale nsembe yamachimo,’+ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. 20 ‘Utenge magazi akewo pangʼono nʼkuwapaka panyanga 4 za guwa lansembe komanso mʼmakona 4 a chigawo chachitatu cha guwalo. Uwapakenso pakakhoma konse kozungulira chigawo chachitatucho kuti uyeretse guwa lansembelo ku machimo ndiponso kuti uliperekere nsembe yophimba machimo.+ 21 Kenako utenge ngʼombe yaingʼono yamphongo ya nsembe yamachimo kuti ansembe akaipsereze pamalo apadera apakachisi, kunja kwa malo opatulika.+ 22 Pa tsiku lachiwiri, udzapereke mbuzi yamphongo yopanda chilema kuti ikhale nsembe yamachimo. Ansembewo adzayeretse guwa lansembelo ku machimo ngati mmene analiyeretsera ku machimo popereka ngʼombe yaingʼono yamphongo.
23 Ukamaliza kuyeretsa guwalo ku machimo, udzabweretse ngʼombe yaingʼono yamphongo yopanda chilema ndi nkhosa yamphongo yopanda chilema kuchokera pagulu la ziweto. 24 Udzazibweretse kwa Yehova ndipo ansembe adzaziwaze mchere+ nʼkuzipereka kwa Yehova monga nsembe yopsereza yathunthu. 25 Tsiku lililonse, kwa masiku 7, uzipereka mbuzi yamphongo monga nsembe yamachimo+ komanso ngʼombe yaingʼono yamphongo ndi nkhosa yamphongo. Nyama zimenezi zizichokera pagulu la ziweto ndipo zizikhala zopanda chilema.* 26 Kwa masiku 7, aphimbe machimo a guwa la nsembe ndipo aliyeretse nʼkuyamba kuligwiritsa ntchito. 27 Masiku 7 amenewo akatha, kuyambira tsiku la 8+ kupita mʼtsogolo, ansembe azidzakuperekerani nsembe* zopsereza zathunthu ndi nsembe zamgwirizano paguwali, ndipo ine ndidzasangalala nanu,’+ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”
44 Munthu uja anandipititsanso kugeti lakunja la malo opatulika, limene linayangʼana kumʼmawa+ ndipo tinapeza kuti linali lotseka.+ 2 Kenako Yehova anandiuza kuti: “Geti ili lipitiriza kukhala lotseka. Silikuyenera kutsegulidwa ndipo munthu aliyense sakuyenera kudzera pageti limeneli chifukwa chakuti Yehova, Mulungu wa Isiraeli, walowa kudzera pageti limeneli.+ Choncho likuyenera kukhala lotseka. 3 Koma mtsogoleri wa anthu azidzakhala mʼkanyumba kapageti kameneka kuti azidzadya chakudya pamaso pa Yehova+ chifukwa iye ndi mtsogoleri. Azidzalowa mmenemo kudzera kukhonde la kanyumbako ndipo azidzatulukiranso komweko.”+
4 Kenako anandipititsa kutsogolo kwa kachisi kudzera pageti lakumpoto. Nditayangʼana ndinaona kuti ulemerero wa Yehova wadzaza mʼkachisi wa Yehova.+ Choncho ndinagwada nʼkuwerama mpaka nkhope yanga pansi.+ 5 Kenako Yehova anandiuza kuti: “Iwe mwana wa munthu, uchite chidwi,* uonetsetse ndipo umvetsere mwatcheru zonse zimene ndikuuze zokhudza malangizo ndi malamulo a kachisi wa Yehova. Uonetsetse khomo lolowera mʼkachisi ndi makomo onse otulukira mʼmalo opatulika.+ 6 Uuze anthu opandukawo, a nyumba ya Isiraeli kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Mwanyanya kuchita zinthu zonyansa, inu a nyumba ya Isiraeli. 7 Mukabweretsa alendo amene ndi osachita mdulidwe wamumtima ndi mdulidwe wa khungu lawo nʼkulowa nawo mʼmalo anga opatulika, iwo amadetsa kachisi wanga. Mumapereka mkate wanga, mafuta ndi magazi, pamene mukuphwanya pangano langa chifukwa cha zonyansa zanu zonse zimene mukuchita. 8 Inu simunasamalire zinthu zanga zopatulika.+ Mʼmalomwake munasankha anthu ena kuti azigwira ntchito zapamalo anga opatulika mʼmalo mwa inu.”
9 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Mlendo aliyense amene akukhala mu Isiraeli yemwe sanachite mdulidwe wamumtima ndi mdulidwe wa khungu, asalowe mʼmalo anga opatulika.”
10 Koma Alevi amene anachoka kwa ine nʼkupita kutali+ pa nthawi imene Aisiraeli anachoka kwa ine nʼkuyamba kutsatira mafano awo onyansa* adzakumana ndi zotsatira za zochita zawo zoipa. 11 Kenako Aleviwo adzakhala atumiki mʼmalo anga opatulika kuti azidzayangʼanira mageti a kachisi+ komanso kutumikira pakachisi. Iwo azidzapha nyama za nsembe zopsereza zathunthu ndi nsembe zina za anthu ndipo adzaimirira pamaso pa anthuwo nʼkumawatumikira. 12 Ine ndalumbira nditakweza dzanja langa kuti ndiwalange chifukwa chakuti ankatumikira anthu pamaso pa mafano awo onyansa. Ndipo anakhala chinthu chopunthwitsa nʼkuchititsa kuti anthu a nyumba ya Isiraeli achimwe.+ Choncho adzakumana ndi zotsatira za zochita zawo,’ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. 13 ‘Sadzayandikira kwa ine kuti anditumikire monga ansembe kapena kuyandikira zinthu zanga zilizonse zoyera kapena zoyera koposa. Iwo adzachita manyazi chifukwa cha zinthu zonyansa zimene anachita. 14 Koma ine ndidzawaika kuti azidzayangʼanira ntchito zapakachisi, kuti azichita utumiki wapakachisi ndi zinthu zonse zimene zikuyenera kuchitika mʼkachisimo.+
15 Ana a Zadoki, omwe ndi Alevi ansembe,+ amene ankagwira ntchito zapamalo anga opatulika pa nthawi imene Aisiraeli anachoka kwa ine,+ ndi amene adzandiyandikire nʼkumanditumikira. Iwo adzaima pamaso panga nʼkundipatsa mafuta+ ndi magazi,’+ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. 16 ‘Iwo ndi amene adzalowe mʼmalo anga opatulika. Adzayandikira tebulo langa kuti anditumikire+ ndipo adzagwira ntchito zimene apatsidwa ponditumikira.+
17 Iwo akalowa mʼtinyumba tamʼmageti a bwalo lamkati, azivala zovala zansalu.+ Akamatumikira mʼtinyumba tamʼmageti a bwalo lamkati kapena mkati mwenimwenimo, asamavale chovala chilichonse cha ubweya wa nkhosa. 18 Iwo azivala nduwira zansalu kumutu kwawo ndi makabudula ansalu aatali.+ Asamavale chovala chilichonse chimene chingachititse kuti atuluke thukuta. 19 Asanapite kubwalo lakunja kumene kuli anthu, azivula zovala zawo zimene anavala potumikira+ nʼkuziika mʼzipinda zodyera zopatulika.*+ Akatero azivala zovala zina kuti asachititse kuti anthu akhale oyera chifukwa cha zovala zawozo. 20 Asamamete mpala kumutu kwawo+ kapena kusiya tsitsi lakumutu kwawo kuti litalike kwambiri. Iwo azingoyepula tsitsi lakumutu kwawo. 21 Ansembe asamamwe vinyo ngati akukalowa mʼbwalo lamkati.+ 22 Iwo asamakwatire mkazi wamasiye kapena amene mwamuna wake anamusiya ukwati.+ Koma angathe kukwatira namwali yemwe ndi mbadwa ya Isiraeli kapena mkazi wamasiye amene anali mkazi wa wansembe.+
23 Iwo aziphunzitsa anthu anga za kusiyana kwa chinthu chopatulika ndi chinthu chomwe si chopatulika. Ndipo aziwaphunzitsanso kusiyana kwa chinthu chodetsedwa ndi chinthu choyera.+ 24 Ngati pali mlandu, iwo ndi amene akuyenera kukhala oweruza+ ndipo aziweruza motsatira malamulo anga.+ Azisunga malamulo ndi malangizo anga okhudza zikondwerero zanga+ zonse ndipo aziyeretsa masabata anga. 25 Iwo asamayandikire munthu aliyense wakufa kuopera kuti angakhale odetsedwa. Koma wansembe akhoza kudzidetsa chifukwa cha bambo ake, mayi ake, mwana wake wamwamuna, mwana wake wamkazi, mchimwene wake kapena mchemwali wake amene ndi wosakwatiwa.+ 26 Ndipo wansembe akamaliza kudziyeretsa, azimuwerengera masiku 7. 27 Pa tsiku limene adzalowe mʼmalo oyera, mʼbwalo lamkati, kuti akatumikire mʼmalo oyerawo, adzapereke nsembe yake yamachimo,’+ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.
28 ‘Ndipo cholowa chawo ndi ichi: Cholowa chawo ndi ine.+ Musawapatse malo alionse mu Isiraeli, chifukwa cholowa chawo ndi ine. 29 Iwowa ndi amene azidzadya nsembe yambewu,+ nsembe yamachimo ndi nsembe yakupalamula+ ndipo chilichonse choperekedwa kwa Mulungu mu Isiraeli chidzakhala chawo.+ 30 Zipatso zonse zabwino kwambiri zoyambirira kucha komanso zopereka zanu za mtundu uliwonse zidzakhala za ansembe.+ Ufa wanu wamisere wa zokolola zanu zoyambirira muziupereka kwa wansembe.+ Zimenezi zidzachititsa kuti anthu amʼnyumba mwanu adalitsidwe.+ 31 Ansembe asamadye mbalame iliyonse kapena nyama iliyonse imene aipeza yakufa kapena imene yakhadzulidwa ndi chilombo.’”+
45 “‘Mukamagawana dzikoli kuti likhale cholowa chanu,+ mudzatenge malo ena nʼkuwapereka kwa Yehova monga gawo loyera.+ Malowo adzakhale mikono 25,000* mulitali ndi mikono 10,000 mulifupi.+ Malo onsewo* adzakhale gawo loyera. 2 Mkati mwa gawo loyeralo mudzakhale malo ofanana mbali zonse kuti adzakhale malo oyera. Malowa adzakhale mikono 500 mbali zonse*+ ndipo kumbali iliyonse kudzakhale malo odyetserako ziweto okwana mikono 50.+ 3 Kuchokera pamalo amenewa, udzayeze malo okwana mikono 25,000 mulitali ndi mikono 10,000 mulifupi. Mʼmalo amenewa mudzakhale malo opatulika amene ndi malo oyera koposa. 4 Malo amenewa adzakhale gawo lopatulika la ansembe mʼdzikoli,+ omwe ndi atumiki apamalo opatulika, amene amayandikira kwa Yehova nʼkumamutumikira.+ Malo amenewa adzakhala oti adzamangepo nyumba zawo komanso adzakhala malo opatulika omangapo kachisi.
5 Kudzakhale malo okwana mikono 25,000 mulitali ndi mikono 10,000 mʼlifupi.+ Malo amenewa adzakhale a Alevi, omwe ndi atumiki apakachisi. Aleviwo adzakhale ndi zipinda 20 zoti azidzadyeramo chakudya.+
6 Mudzapereke malo okwana mikono 25,000 mulitali (mofanana ndi chopereka chopatulika) ndi mikono 5,000 mulifupi+ kuti adzakhale malo a mzinda. Malo amenewa adzakhale a anthu a nyumba yonse ya Isiraeli.
7 Malo a mtsogoleri wa anthu adzakhale kumbali zonse za chopereka chopatulika komanso za malo amene aperekedwa kuti akhale a mzinda. Adzayandikane ndi chopereka chopatulika komanso malo a mzindawo. Malo a mtsogoleriwo adzakhale kumadzulo ndi kumʼmawa. Mulitali mwake kuchokera kumalire akumadzulo kukafika kumalire akumʼmawa adzakhale ofanana ndi kutalika kwa gawo la fuko la Isiraeli limene layandikana nawo.+ 8 Malo amenewa adzakhale cholowa cha mtsogoleriyo mu Isiraeli. Atsogoleri anga sadzazunzanso anthu anga+ ndipo adzagawa dzikoli kwa anthu a nyumba ya Isiraeli mogwirizana ndi mafuko awo.’+
9 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Ndatopa nanu inu atsogoleri a Isiraeli!
Siyani ziwawa ndi kupondereza anthu anga ndipo muzichita zinthu motsatira malamulo komanso mwachilungamo.+ Lekani kulanda zinthu za anthu anga,’+ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. 10 ‘Muzigwiritsa ntchito masikelo olondola, muyezo wa efa* wolondola ndi mitsuko* yoyezera yolondola.+ 11 Muyezo wa efa komanso wa mtsuko woyezera uzikhala wosasinthasintha. Muyezo wa mtsuko uzikhala wokwana gawo limodzi la magawo 10 a homeri* ndipo muyezo wa efa uzikhala wokwana gawo limodzi la magawo 10 a homeri. Muyezo wa homeri ukhale muyezo wa nthawi zonse. 12 Sekeli*+ imodzi izikwana magera* 20. Muziphatikiza masekeli 20, masekeli 25 ndi masekeli 15 kuti ukhale muyezo wanu umodzi wa mane.*
13 Muzipereka zinthu izi kuti chikhale chopereka chanu: Pa tirigu wanu wokwana homeri, muzipereka gawo limodzi mwa magawo 6 a muyezo wa efa. Ndipo pa balere wanu wokwana homeri muzipereka gawo limodzi mwa magawo 6 a muyezo wa efa. 14 Poyeza mafuta oti muzipereka, muzigwiritsa ntchito mtsuko woyezera. Mtsuko woyezera ndi wokwana gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa kori.* Mitsuko 10 ndi yokwana homeri chifukwa mitsuko 10 imakwana homeri imodzi. 15 Pa ziweto zonse mu Isiraeli, muzipereka nkhosa imodzi kuchokera pa nkhosa 200 zilizonse. Muzidzagwiritsa ntchito zinthu zonsezi popereka nsembe zambewu,+ nsembe zopsereza zathunthu+ ndi nsembe zamgwirizano+ pofuna kuphimba machimo a anthu,’+ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.
16 ‘Anthu onse amʼdzikoli azidzapereka zopereka zimenezi+ kwa mtsogoleri mu Isiraeli. 17 Koma mtsogoleri ndi amene adzakhale ndi udindo woyangʼanira nsembe zopsereza zathunthu,+ nsembe yambewu+ ndi nsembe yachakumwa. Iye azidzayangʼanira nsembezo pa nthawi ya zikondwerero,+ pa masiku amene mwezi watsopano waoneka, pa masiku a Sabata+ ndi pa nthawi ya zikondwerero zonse za nyumba ya Isiraeli.+ Mtsogoleriyo ndi amene azidzapereka kwa ansembe nsembe yamachimo, nsembe yambewu, nsembe yopsereza yathunthu ndi nsembe zamgwirizano kuti aphimbe machimo a nyumba ya Isiraeli.’
18 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: ‘Mʼmwezi woyamba, pa tsiku loyamba la mweziwo, uzitenga ngʼombe yamphongo yaingʼono yopanda chilema kuchokera pagulu la ziweto, ndipo uziyeretsa kachisi ku machimo.+ 19 Wansembe azitenga ena mwa magazi a nsembe yamachimo nʼkuwapaka pafelemu la kachisi,+ mʼmakona 4 a chigawo chachitatu cha guwa lansembe komanso pafelemu la kanyumba kapageti ka bwalo lamkati. 20 Muzichita zimenezi pa tsiku la 7 la mweziwo chifukwa cha munthu aliyense amene wachimwa mwangozi kapena mosadziwa+ ndipo muziyeretsa kachisi ku machimo.+
21 Mʼmwezi woyamba, pa tsiku la 14 la mweziwo, muzichita chikondwerero cha Pasika.+ Kwa masiku 7 muzidya mikate yopanda zofufumitsa.+ 22 Pa tsiku limeneli, mtsogoleri azipereka kwa ansembe ngʼombe yaingʼono yamphongo kuti ikhale nsembe yamachimo ake komanso a anthu onse amʼdzikoli.+ 23 Kwa masiku 7 a chikondwererocho, iye azipereka kwa ansembe nyama zoti ziperekedwe kwa Yehova ngati nsembe yopsereza yathunthu. Azipereka ngʼombe 7 zazingʼono zamphongo ndi nkhosa 7 zamphongo. Nyama zimenezi zizikhala zopanda chilema ndipo azizipereka tsiku lililonse kwa masiku 7 amenewo.+ Aziperekanso mbuzi yamphongo tsiku lililonse kuti ikhale nsembe yamachimo. 24 Popereka ngʼombe iliyonse yaingʼono yamphongo aziperekanso nsembe yambewu yokwana muyezo umodzi wa efa. Popereka nkhosa iliyonse yamphongo aziperekanso nsembe yambewu yokwana muyezo umodzi wa efa. Pa muyezo uliwonse wa efa azipereka mafuta okwana muyezo umodzi wa hini.*
25 Mʼmwezi wa 7, kuyambira pa tsiku la 15 la mweziwo, kwa masiku 7 pa nthawi ya chikondwerero,+ mtsogoleri azipereka kwa wansembe zinthu zofanana ndi zimenezi. Azipereka zinthu zimenezi kuti zikhale nsembe yamachimo, nsembe zopsereza zathunthu, nsembe yambewu ndiponso mafuta.’”
46 “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: ‘Kanyumba kapageti la bwalo lamkati kamene kayangʼana kumʼmawa+ kazikhala kotseka+ kwa masiku 6 ogwira ntchito.+ Koma pa tsiku la Sabata ndi pa tsiku limene mwezi watsopano waoneka kazitsegulidwa. 2 Mtsogoleri azilowa kuchokera panja kudzera pakhonde la kanyumba kapagetiko+ ndipo aziima pafupi ndi felemu lagetilo. Ndiyeno ansembe azimuperekera nsembe yopsereza yathunthu ndi nsembe zake zamgwirizano. Mtsogoleriyo azigwada nʼkuwerama pakhomo la kanyumba kapageti kenako nʼkutuluka. Koma getilo lisamatsekedwe mpaka madzulo. 3 Anthu amʼdzikoli azigwadanso nʼkuwerama pamaso pa Yehova pakhomo lolowera mʼkanyumba kameneka pa masiku a Sabata ndi pa masiku amene mwezi watsopano waoneka.+
4 Nsembe yopsereza yathunthu imene mtsogoleri wa anthu azipereka kwa Yehova pa tsiku la Sabata, izikhala ana a nkhosa amphongo 6 ndi nkhosa yamphongo imodzi. Nyama zonsezi zizikhala zopanda chilema.+ 5 Popereka nkhosa yamphongo aziperekanso nsembe yambewu yokwana muyezo umodzi wa efa.* Popereka ana a nkhosa amphongo aziperekanso nsembe yambewu imene angakwanitse. Pa nsembe iliyonse yambewu yokwana muyezo wa efa azipereka mafuta okwana muyezo wa hini.*+ 6 Pa tsiku limene mwezi watsopano waoneka, azipereka ngʼombe yaingʼono yamphongo yopanda chilema kuchokera pagulu la ziweto. Aziperekanso ana a nkhosa amphongo 6 ndi nkhosa imodzi yamphongo. Nyama zonsezi zizikhala zopanda chilema.+ 7 Popereka ngʼombe yaingʼono yamphongo aziperekanso nsembe yambewu yokwana muyezo umodzi wa efa. Akamapereka nkhosa yamphongo aziperekanso nsembe yambewu yokwana muyezo umodzi wa efa. Popereka ana a nkhosa amphongo aziperekanso nsembe yambewu imene angakwanitse. Pa nsembe iliyonse yambewu yokwana muyezo wa efa, azipereka mafuta okwana muyezo wa hini.
8 Mtsogoleri wa anthu akamalowa, azidzera mbali yakukhonde ya kanyumba kapageti ndipo akamatuluka azidzeranso komweko.+ 9 Anthu amʼdzikoli akafika pamaso pa Yehova pa nthawi ya zikondwerero,+ anthu amene alowa kudzalambira kudzera pageti la kumpoto+ azidzatulukira pageti lakumʼmwera.+ Amene alowera pageti lakumʼmwera azidzatulukira pageti lakumpoto. Munthu aliyense asadzatulukire pageti limene analowera chifukwa aliyense akuyenera kutulukira pageti limene lili kutsogolo kwake. 10 Anthuwo akamalowa, mtsogoleri amene ali pakati pawo azilowa nawo limodzi, ndipo akamatuluka nayenso azituluka. 11 Mukamachita zikondwerero komanso pa nthawi ya zikondwerero zanu, azipereka ngʼombe yaingʼono yamphongo pamodzi ndi nsembe yambewu yokwana muyezo umodzi wa efa. Aziperekanso nkhosa yamphongo pamodzi ndi nsembe yambewu yokwana muyezo umodzi wa efa. Akamapereka ana a nkhosa amphongo aziperekanso nsembe yambewu imene angakwanitse. Pa nsembe iliyonse yambewu yokwana muyezo wa efa azipereka mafuta okwana muyezo wa hini.+
12 Ngati mtsogoleri wa anthu akupereka kwa ansembe nsembe yopsereza yathunthu+ kapena nsembe zamgwirizano kuti zikhale nsembe yaufulu yoperekedwa kwa Yehova, azimutsegulira geti lakumʼmawa. Mtsogoleriyo azipereka kwa ansembe nsembe yake yopsereza yathunthu ndi nsembe zake zamgwirizano ngati mmene amachitira pa tsiku la Sabata.+ Akatuluka getilo lizitsekedwa.+
13 Tsiku lililonse muzipereka kwa Yehova mwana wa nkhosa wamphongo wopanda chilema wosakwanitsa chaka kuti ikhale nsembe yopsereza yathunthu.+ Muzichita zimenezi mʼmawa uliwonse. 14 Mukamapereka mwana wa nkhosayo, muziperekanso nsembe yambewu mʼmawa uliwonse yokwanira gawo limodzi mwa magawo 6 a muyezo wa efa. Muziperekanso mafuta okwana gawo limodzi mwa magawo atatu a muyezo wa hini kuti aziwazidwa mu ufa wosalala monga nsembe yambewu imene iziperekedwa kwa Yehova nthawi zonse. Limeneli ndi lamulo limene lidzakhalepo mpaka kalekale. 15 Mʼmawa uliwonse, iwo azipereka kwa ansembe mwana wa nkhosa wamphongo, nsembe yambewu komanso mafuta, kuti zikhale nsembe yopsereza yathunthu ya nthawi zonse.’
16 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: ‘Mtsogoleri wa anthu akapereka mphatso kwa mwana wake aliyense wamwamuna monga cholowa chake, mphatsoyo idzakhala chuma cha ana akewo. Chimenecho ndi chuma cha anawo ndipo chidzakhala cholowa chawo. 17 Koma akapereka mphatso kwa mmodzi wa antchito ake kuchokera pacholowa chake, mphatsoyo idzakhala ya wantchitoyo mpaka chaka cha ufulu,+ kenako idzabwezedwa kwa mtsogoleriyo. Koma cholowa chimene wapereka kwa ana ake chidzakhala chawo mpaka kalekale. 18 Mtsogoleri wa anthu asamakakamize munthu aliyense kuti achoke pamalo omwe ndi cholowa chake nʼkutenga malowo kuti akhale ake. Ana ake aamuna aziwapatsa cholowa kuchokera pamalo amene ali nawo, kuti pakati pa anthu anga pasapezeke munthu aliyense amene wathamangitsidwa pamalo ake.’”
19 Kenako munthu uja anandilowetsa mkati kudzera pakhomo+ limene lili pafupi ndi geti lopita kunyumba zopatulika* zomwe ansembe ankadyeramo, zimene zinayangʼana kumpoto.+ Kumeneko ndinaona malo kumbuyo, mbali yakumadzulo. 20 Ndiyeno munthu uja anandiuza kuti: “Awa ndi malo amene ansembe aziwiritsirapo nsembe yakupalamula ndi nsembe yamachimo komanso pamene aziphikirapo nsembe yambewu.+ Aziphikira pamenepa kuti asamatulutse chilichonse kupita nacho kubwalo lakunja nʼkuchititsa kuti anthu akhale oyera.”+
21 Kenako anandipititsa mʼbwalo lakunja nʼkundidutsitsa mʼmakona 4 a bwalolo ndipo ndinaona kuti pakona iliyonse ya bwalo lakunjalo panali bwalo. 22 Mʼmakona onse 4 a bwalolo munali mabwalo angʼonoangʼono amene anali mikono 40* mulitali ndi mikono 30 mulifupi. Mabwalo 4 onsewo anali aakulu mofanana.* 23 Panali kakhoma kuzungulira mkati monse mwa tinyumba tonse 4 tapakonato. Mʼmunsi mwa timakoma timeneto anamangamo malo oti aziwiritsirapo nsembe. 24 Kenako anandiuza kuti: “Izi ndi nyumba zimene atumiki apakachisi amawiritsiramo nsembe zimene anthu amapereka.”+
47 Kenako anandipititsanso kukhomo lolowera mʼkachisi+ ndipo kumeneko ndinaona madzi akutuluka pansi pakhomo la kachisi+ nʼkumalowera chakumʼmawa, chifukwa kachisiyo anayangʼana kumʼmawa. Madziwo ankatuluka pansi kuchokera kumbali yakumanja kwa kachisiyo, kumʼmwera kwa guwa lansembe.
2 Ndiyeno ananditulutsa kudzera pageti lakumpoto+ ndipo anandipititsa kunja nʼkuzungulira kukafika kugeti lakunja limene linayangʼana kumʼmawa.+ Kumeneko ndinaonako madzi akuyenda kuchokera kumbali yakumanja kwa getilo.
3 Munthu uja anapita mbali yakumʼmawa atatenga chingwe choyezera mʼmanja mwake.+ Kenako anayeza mtsinjewo mikono* 1,000 kuchokera pakanyumba kapageti, ndipo anandiuza kuti ndiwoloke mtsinjewo. Madzi ake anali olekeza mʼmapazi.
4 Kenako anayezanso mtsinjewo mikono ina 1,000 ndipo anandiuza kuti ndiwoloke. Madzi ake anali olekeza mʼmawondo.
Anayezanso mtsinjewo mikono ina 1,000 nʼkundiuza kuti ndiwoloke ndipo madzi ake anali olekeza mʼchiuno.
5 Atayezanso mtsinjewo mikono ina 1,000, mtsinjewo unakula kwambiri moti sindinathe kuwoloka chifukwa chakuti madzi ake anali ozama kwambiri moti munthu amafunika kusambira. Unali mtsinje waukulu woti munthu sakanatha kuwoloka.
6 Ndiyeno anandifunsa kuti: “Iwe mwana wa munthu, kodi waona zimenezi?”
Kenako munthu uja ananditulutsa mʼmadzimo nʼkupita nane mʼmphepete mwa mtsinjewo. 7 Nditatuluka mʼmadzimo ndinaona kuti mʼmphepete mwa mtsinjewo munali mitengo yambirimbiri mbali zonse.+ 8 Ndiyeno anandiuza kuti: “Madzi awa akupita kuchigawo cha kumʼmawa ndipo adutsa ku Araba*+ nʼkukafika kunyanja. Madziwa akakafika kunyanjako,+ akachititsa kuti madzi amʼnyanjamo akhale abwino. 9 Kulikonse kumene madziwo apita,* zamoyo zamʼmadzi za mtundu uliwonse zidzakhala ndi moyo. Nsomba zidzachuluka chifukwa madzi amenewa adzafika kunyanja. Madzi amʼnyanja adzakhala abwino ndipo kulikonse kumene mtsinjewo ukupita, chilichonse chidzakhala ndi moyo.
10 Asodzi adzaima mʼmbali mwa nyanjayo kuchokera ku Eni-gedi+ mpaka ku Eni-egilaimu, kumene kudzakhale malo oyanikapo makoka. Kudzakhala nsomba zambirimbiri zamitundu yosiyanasiyana ngati nsomba za ku Nyanja Yaikulu.*+
11 Madzi amʼzithaphwi ndi mʼmadambo amʼmphepete mwa nyanjayo sadzasintha nʼkukhala abwino. Madzi amenewo adzakhalabe amchere.+
12 Kumbali zonse zamʼmphepete mwa mtsinjewo mudzamera mitengo yosiyanasiyana ya zipatso. Masamba ake sadzafota ndipo zipatso zake sizidzatha. Mwezi uliwonse mitengoyo izidzabereka zipatso chifukwa chakuti madzi ake akuchokera kumalo opatulika.+ Zipatso zake zidzakhala chakudya ndipo masamba ake adzakhala mankhwala.”+
13 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Limeneli ndi dera limene mudzagawire mafuko 12 a Isiraeli ngati cholowa chawo ndipo zigawo ziwiri zidzakhale za mbadwa za Yosefe.+ 14 Mudzatenge dzikoli kuti likhale cholowa chanu ndipo aliyense adzalandire gawo lofanana ndi la mnzake. Ine ndinalumbira kuti ndidzapereka dziko limeneli kwa makolo anu+ ndipo tsopano ndikulipereka kwa inu kuti likhale cholowa chanu.
15 Malire a dzikoli kumbali yakumpoto ndi awa: Akuyambira ku Nyanja Yaikulu kudzera njira ya ku Heteloni+ nʼkumalowera ku Zedadi,+ 16 ku Hamati,+ ku Berota,+ ku Siburaimu, amene ali pakati pa dera la Damasiko ndi dera la Hamati, mpaka kukafika ku Hazere-hatikoni kufupi ndi malire a Haurani.+ 17 Choncho malirewo adzayambire kunyanja mpaka ku Hazara-enoni,+ kumene ndi kumalire akumpoto kwa Damasiko komanso kumalire a Hamati.+ Amenewa ndi malire akumpoto.
18 Malire a mbali yakumʼmawa ali pakati pa Haurani ndi Damasiko, kudutsa mʼmbali mwa mtsinje wa Yorodano pakati pa Giliyadi+ ndi dziko la Isiraeli. Mudzayeze mtunda wochokera kumalirewo kukafika kunyanja yakumʼmawa.* Amenewa ndi malire akumʼmawa.
19 Malire a mbali yakumʼmwera, adzayambire ku Tamara kukafika kumadzi a Meribati-kadesi,+ kenako akafike kuchigwa cha Iguputo mpaka ku Nyanja Yaikulu.+ Amenewa ndi malire akumʼmwera.
20 Kumbali yakumadzulo malire anu ndi Nyanja Yaikulu, kuchokera mʼmalire a mbali yakumʼmwera mpaka kukafika malo amene ayangʼanizana ndi Lebo-hamati.*+ Amenewa ndi malire akumadzulo.
21 Inu mugawane dzikoli pakati pa mafuko onse 12 a Isiraeli. 22 Mugawane dzikoli kuti likhale cholowa chanu ndi cha alendo omwe akukhala pakati panu, amene abereka ana pa nthawi imene amakhala nanu. Kwa inu, alendowo akhale ngati nzika za Isiraeli. Iwo alandire cholowa pamodzi ndi inu pakati pa mafuko a Isiraeli. 23 Mlendo aliyense muzimupatsa cholowa mʼdera la fuko limene akukhala,” akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.
48 “Magawo amene mafuko adzalandire potsatira mayina awo, kuyambira kumalire akumpoto ndi awa: Gawo la fuko la Dani+ likhale mʼmbali mwa msewu wa ku Heteloni wopita ku Lebo-hamati*+ mpaka kukafika ku Hazara-enani, kumalire akumpoto a Damasiko kufupi ndi Hamati.+ Gawolo liyambire kumalire akumʼmawa kukafika kumalire akumadzulo. 2 Gawo la fuko la Aseri+ lichite malire ndi gawo la fuko la Dani, kuyambira kumalire akumʼmawa kukafika kumalire akumadzulo. 3 Gawo la fuko la Nafitali+ lichite malire ndi gawo la fuko la Aseri, kuyambira kumalire akumʼmawa kukafika kumalire akumadzulo. 4 Gawo la fuko la Manase+ lichite malire ndi gawo la fuko la Nafitali, kuyambira kumalire akumʼmawa kukafika kumalire akumadzulo. 5 Gawo la fuko la Efuraimu lichite malire ndi gawo la fuko la Manase,+ kuyambira kumalire akumʼmawa kukafika kumalire akumadzulo. 6 Gawo la fuko la Rubeni lichite malire ndi gawo la fuko la Efuraimu,+ kuyambira kumalire akumʼmawa kukafika kumalire akumadzulo. 7 Gawo la fuko la Yuda lichite malire ndi gawo la fuko la Rubeni,+ kuyambira kumalire akumʼmawa kukafika kumalire akumadzulo. 8 Mupereke gawo lina kuti likhale chopereka chanu. Gawolo lichite malire ndi gawo la fuko la Yuda kuyambira kumalire akumʼmawa kukafika kumalire akumadzulo ndipo likhale mikono 25,000* mulifupi.+ Mulitali mwake lifanane ndi magawo a mafuko aja kuyambira kumalire akumʼmawa kukafika kumalire akumadzulo. Malo opatulika akhale pakati pa gawo limeneli.
9 Gawo loti mupereke kwa Yehova monga chopereka chanu likhale mikono 25,000 mulitali ndi mikono 10,000 mulifupi. 10 Gawo limeneli likhale chopereka chopatulika cha ansembe.+ Mbali yakumpoto, gawoli likhale mikono 25,000. Mbali yakumadzulo likhale mikono 10,000. Mbali yakumʼmawa likhale mikono 10,000 ndipo mbali yakumʼmwera likhale mikono 25,000. Malo opatulika a Yehova adzakhala pakati pa gawo limeneli. 11 Gawo limeneli likhale la ansembe opatulika, ana a Zadoki,+ amene ankanditumikira ndipo sanandisiye pamene Aisiraeli ndi Alevi anandisiya.+ 12 Ansembewo akhale ndi gawo lawo kuchokera pa gawo limene mwapereka kuti likhale gawo lopatulika koposa, ndipo lichite malire ndi gawo la Alevi.
13 Alevi akhale ndi gawo pafupi ndi gawo la ansembe. Mulitali mwake likhale mikono 25,000 ndipo mulifupi likhale mikono 10,000. (Malo onsewo akhale aatali mikono 25,000 ndipo mulifupi mwake akhale okwana mikono 10,000.) 14 Aleviwo asamagulitse, kusinthanitsa kapena kupereka kwa munthu wa fuko lina mbali iliyonse ya malo abwino kwambiriwo, chifukwa malo amenewo ndi opatulika kwa Yehova.
15 Malo otsala okwana mikono 5,000 mulifupi ndi mikono 25,000 mulitali, akhale malo a mzinda oti munthu aliyense angagwiritse ntchito.+ Malo amenewa akhale oti anthu azimangako nyumba komanso kudyetserako ziweto. Mzinda ukhale pakati pa malowa.+ 16 Miyezo ya mzindawo ndi iyi: Mbali yakumpoto ikhale mikono 4,500. Mbali yakumʼmwera ikhale mikono 4,500. Mbali yakumʼmawa ikhale mikono 4,500, ndipo mbali yakumadzulo ikhalenso mikono 4,500. 17 Malo odyetserako ziweto a mzindawo akhale mikono 250 mbali yakumpoto, mikono 250 mbali yakumʼmwera, mikono 250 mbali yakumʼmawa komanso mikono 250 mbali yakumadzulo.
18 Malo otsala akhale aatali mofanana ndi malo omwe ndi chopereka chopatulika.+ Akhale mikono 10,000 kumʼmawa ndiponso mikono 10,000 kumadzulo. Malo amenewo achite malire ndi malo omwe ndi chopereka chopatulika. Zokolola zapamalowo zizikhala chakudya cha amene akugwira ntchito mumzindawo. 19 Anthu ochokera mʼmafuko onse a Isiraeli amene akugwira ntchito mumzinda ndi omwe azidzalima malo amenewa.+
20 Malo onse oti aperekedwe akhale mikono 25,000 mbali zonse 4. Mupereke malo amenewa kuti akhale chopereka chopatulika ndiponso malo a mzinda.
21 Malo amene atsala kumbali zonse za chopereka chopatulika ndiponso ya malo a mzinda akhale a mtsogoleri wa anthu.+ Malowa adzachita malire ndi malo omwe ndi chopereka, amene akukwana mikono 25,000 kumʼmawa ndi kumadzulo. Malowo achite malire ndi malo amene anaperekedwa aja ndipo akhale a mtsogoleri wa anthu. Malo omwe ndi chopereka chopatulika komanso malo opatulika a kachisi aja akhale pakati pa malo a mtsogoleriwa.
22 Malo a Alevi komanso malo a mzinda akhale pakati pa malo a mtsogoleri. Malo a mtsogoleriwo achite malire ndi gawo la fuko la Yuda+ komanso gawo la fuko la Benjamini.
23 Pa mafuko ena otsalawo, gawo la fuko la Benjamini liyambire kumalire akumʼmawa kukafika kumalire akumadzulo.+ 24 Gawo la fuko la Simiyoni lichite malire ndi gawo la fuko la Benjamini,+ kuyambira kumalire akumʼmawa kukafika kumalire akumadzulo. 25 Gawo la fuko la Isakara+ lichite malire ndi gawo la fuko la Simiyoni, kuyambira kumalire akumʼmawa kukafika kumalire akumadzulo. 26 Gawo la fuko la Zebuloni lichite malire ndi gawo la fuko la Isakara,+ kuyambira kumalire akumʼmawa kukafika kumalire akumadzulo.+ 27 Gawo la fuko la Gadi lichite malire ndi gawo la fuko la Zebuloni,+ kuyambira kumalire akumʼmawa kukafika kumalire akumadzulo. 28 Malire akumʼmwera a dzikolo akhale malire a gawo la fuko la Gadi ndipo achokere ku Tamara+ kukafika kumadzi a Meribati-kadesi,+ kuchigwa cha Iguputo+ mpaka ku Nyanja Yaikulu.*
29 Limeneli ndi dziko lomwe mukuyenera kugawa kwa mafuko onse a Isiraeli kuti likhale cholowa chawo+ ndipo magawo awo akhale amenewa,”+ akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.
30 “Makomo otulukira mumzinda akhale motere: Kumbali yakumpoto mzindawo ukhale mikono 4,500.+
31 Mayina a mageti a mzindawo akhale ofanana ndi mayina a mafuko a Isiraeli. Mbali yakumpoto kukhale mageti atatu. Geti limodzi likhale ndi dzina lakuti Rubeni, geti lina Yuda ndipo lina Levi.
32 Kumbali yakumʼmawa mzindawo ukhale mikono 4,500 ndipo kukhale mageti atatu awa: Geti limodzi likhale ndi dzina lakuti Yosefe, geti lina Benjamini ndipo lina Dani.
33 Kumbali yakumʼmwera mzindawo ukhale mikono 4,500 ndipo kukhale mageti atatu awa: Geti limodzi likhale ndi dzina lakuti Simiyoni, geti lina Isakara ndipo lina Zebuloni.
34 Kumbali yakumadzulo mzindawo ukhale mikono 4,500 ndipo kukhale mageti awa: Geti limodzi likhale ndi dzina lakuti Gadi, geti lina Aseri ndipo geti lina Nafitali.
35 Kuzungulira mzindawo pakhale mtunda wokwana mikono 18,000. Kuyambira tsiku limenelo, dzina la mzindawo lidzakhala lakuti, Yehova Ali Kumeneko.”+
Kutanthauza, “Mulungu Amapereka Mphamvu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Dzanja la Yehova linafika pa iye.”
Kapena kuti, “mphezi.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “zamoyo 4.”
Zikuoneka kuti wilo limodzi linali mkati mwa wilo linzake mopingasa.
Amenewa ndi malo oyamba pa malo 93 pamene mawu amenewa akupezeka mʼbuku la Ezekieli.
Mabaibulo ena amati, “ngakhale kuti ndi anthu osamva ndipo ali ngati zinthu zokulasa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “idya chimene wapeza.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “pakati pa ana a anthu ako.”
Kapena kuti, “koma magazi ake ndidzawafuna kuchokera kwa iwe.”
Kapena kuti, “nʼkumachita zopanda chilungamo.”
Kapena kuti, “ndidzakuimba mlandu chifukwa cha magazi ake.”
Sipeloti ndi mtundu wina wa tirigu koma wosakoma.
Pafupifupi magalamu 230. Onani Zakumapeto B14.
Mʼchilankhulo choyambirira, “gawo limodzi la magawo 6 a muyezo wa hini,” lomwe ndi pafupifupi hafu ya 1 lita. Onani Zakumapeto B14.
Mʼchilankhulo choyambirira, “ndidzathyola ndodo za mkate.” Nʼkutheka kuti akutanthauza ndodo zimene ankagwiritsira ntchito posunga mikate.
Kapena kuti, “ndidzakuchepetsa.”
Kapena kuti, “matenda.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ndidzathyola ndodo za mkate.” Nʼkutheka kuti akutanthauza ndodo zimene ankagwiritsira ntchito posunga mikate.
Mawu a Chiheberi ali ndi tanthauzo lofanana ndi mawu akuti “ndowe” ndipo amagwiritsidwa ntchito posonyeza kuipidwa.
Kapena kuti, “wachiwerewere.”
Mabaibulo ena amati, “Inu anthu amene mukukhala mʼdzikoli, nkhata yamaluwa ya tsoka ikubwera.”
Mabaibulo ena amati, “Nkhata yamaluwa ya tsoka ikubwera.”
Apa akutanthauza kuti anthu amene amagula kapena kugulitsa zinthu sadzapindula chifukwa onsewo adzawonongedwa.
Mabaibulo ena amati, “pochita zolakwa.”
Kutanthauza kuti adzakodzedwa chifukwa cha mantha.
Kutanthauza kuti adzametedwa tsitsi chifukwa cha chisoni.
Kutanthauza zinthu zawo zopangidwa ndi golide komanso siliva.
Kutanthauza siliva ndi golide wawo amene anagwiritsa ntchito popanga mafano.
Zikuoneka kuti akunena malo amkati kwambiri a nyumba yopatulika ya Yehova.
Kapena kuti, “malangizo.”
Mawu a Chiheberi ali ndi tanthauzo lofanana ndi mawu akuti “ndowe” ndipo amagwiritsidwa ntchito posonyeza kuipidwa.
Zikuoneka kuti nthambi imeneyi ankaigwiritsa ntchito polambira mafano.
Kapena kuti, “lamkuwa.”
Umenewu ndi mzinda wa Yerusalemu umene Ayuda ankaona ngati azikhalamo motetezeka.
Kapena kuti, “mphika wakukamwa kwakukulu.”
Kutanthauza mtima wofuna kutsogoleredwa ndi Mulungu.
Kapena kuti, “kwachinyengo.”
Iwo ankachita zimenezi kuti khomalo lizioneka ngati lolimba.
Mʼchilankhulo choyambirira, “ndipo inu matalala akuluakulu, mudzagwanso.”
Kutanthauza zithumwa zovala mʼmanja kapena mʼzigongono.
Kapena kuti, “azimva ululu.”
Mawu a Chiheberi ali ndi tanthauzo lofanana ndi mawu akuti “ndowe” ndipo amagwiritsidwa ntchito posonyeza kuipidwa.
Mʼchilankhulo choyambirira, “Ndidzachititsa kuti mantha agwire mitima ya Aisiraeli.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ndidzathyola ndodo za mkate.” Nʼkutheka kuti akutanthauza ndodo zimene ankagwiritsira ntchito posunga mikate.
Kapena kuti, “ziweruzo zanga zowononga.”
Kapena kuti, “chikopa cha katumbu.”
Kapena kuti, “kukhala wolamulira.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Dzina lako linatchuka.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “kafungo kokhazika mtima pansi.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “pokhanyulira munthu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “anthu oyandikana nawo a ziwalo zikuluzikulu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “dziko la Kanani.”
Mabaibulo ena amati, “Iweyo wandikwiyitsa koopsa chifukwa cha zonse zimene wakhala ukuchitazi.”
Mawu a Chiheberi ali ndi tanthauzo lofanana ndi mawu akuti “ndowe” ndipo amagwiritsidwa ntchito posonyeza kuipidwa.
Mʼchilankhulo choyambirira, “kumanzere kwako.”
Nʼkutheka kuti apa akunena za matauni ozungulira.
Mʼchilankhulo choyambirira, “kumanja kwako.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “kudziko la Kanani.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”
Ameneyu ndi Nebukadinezara.
Kutanthauza Zedekiya.
Mʼchilankhulo choyambirira, “anapereka dzanja lake.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “kumphepo zonse.”
Kapena kuti, “Munthu amene wachimwa ndi amene adzafe.”
Mawu a Chiheberi ali ndi tanthauzo lofanana ndi mawu akuti “ndowe” ndipo amagwiritsidwa ntchito posonyeza kuipidwa.
Kapena kuti, “Munthu amene akuchimwayo ndi amene adzafe.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Zolakwa zake sizidzakumbukiridwa.”
Kapena kuti, “nʼkumachita zopanda chilungamo.”
Kapena kuti, “nʼkumachita zopanda chilungamo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ndipo mudzipangire mtima watsopano.”
Kapena kuti, “mikango yaingʼono yamanyenje.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mtengo wa mpesa umene uli mʼmagazi anu.”
Kapena kuti, “Ndodo.”
Kapena kuti, “kundodo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ndinakweza dzanja langa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”
Kapena kuti, “ndinaliyendera kuti iwo akakhalemo.”
Mawu a Chiheberi ali ndi tanthauzo lofanana ndi mawu akuti “ndowe” ndipo amagwiritsidwa ntchito posonyeza kuipidwa.
Kutanthauza Aisiraeli.
Kutanthauza Aisiraeli.
Mʼchilankhulo choyambirira, “kafungo kokhazika mtima pansi.”
Kapena kuti, “kuchita uhule ndi mafanowo.”
Kapena kuti, “amatumikira.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “kafungo kokhazika mtima pansi.”
Kutanthauza kuti adzakodzedwa chifukwa cha mantha.
Mʼchilankhulo choyambirira, “mkono wolozera.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “aterafi ake.”
Apa akutanthauza anthu okhala ku Yerusalemu.
Mʼchilankhulo choyambirira, “adzakugwirani pamkono.”
Kapena kuti, “chisoti chachifumu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “inu mudzaunjikidwa pamakosi a anthu ophedwa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “kumalo amene munalengedwera.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “kodi uweruza, kodi uweruza mzinda.”
Mawu a Chiheberi ali ndi tanthauzo lofanana ndi mawu akuti “ndowe” ndipo amagwiritsidwa ntchito posonyeza kuipidwa.
Mʼchilankhulo choyambirira, “amavula bambo awo.”
Kapena kuti, “akupatse katapira.”
Kapena kuti, “mkuwa.”
Kutanthauza, “Tenti Yake.”
Kutanthauza, “Tenti Yanga Ili mwa Iye.”
Mawu a Chiheberi ali ndi tanthauzo lofanana ndi mawu akuti “ndowe” ndipo amagwiritsidwa ntchito posonyeza kuipidwa.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mʼchilankhulo choyambirira, “oitanidwa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “wandiponya kumbuyo.”
Kutanthauza kuti anachita chigololo polambira mafano.
Mʼchilankhulo choyambirira, “dzina la tsikuli.”
Kapena kuti, “mphika wa kukamwa kwakukulu.”
Kapena kuti, “wamkuwa.”
Kapena kuti, “Koma iwe usadzigugude pachifuwa.”
Kapena kuti, “mʼmalo otsetsereka a Mowabu.”
Kapena kuti, “mizinda imene imakongoletsa dzikolo.”
Kapena kuti, “moipidwa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Ana ake aakazi amene ali.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Nebukadirezara.” Kameneka ndi kalembedwe kena ka dzinali.
Kapena kuti, “chida chake chankhondo.”
Kapena kuti, “malupanga ake.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “anthu amene akufa.”
Kapena kuti, “Atsogoleri.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “malaya odula manja.”
Kapena kuti, “mʼmanda.”
Kapena kuti, “ndidzakongoletsa.”
Mtengo wa junipa ndi wofanana ndi mtengo wa mkungudza.
Mʼchilankhulo choyambirira, “Amuna achikulire.”
Kapena kuti, “msonkho.” Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mtengo umenewu uli mʼgulu limodzi ndi mtengo wa sinamoni.
Mabaibulo ena amati, “unali ndi ulemerero.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Mpingo wonse umene uli mwa iwe.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “wakhala chete.”
Kapena kuti, “mʼmanda.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “bango.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “chiuno chawo chinjenjemere.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “iye wanena kuti.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Nebukadirezara.” Kameneka ndi kalembedwe kena ka dzinali.
Mʼchilankhulo choyambirira, “Nebukadirezara.” Kameneka ndi kalembedwe kena ka dzinali.
Kapena kuti, “nyumba ya Isiraeli ndidzaipatsa mphamvu.”
Nʼkutheka kuti akunena za Aisiraeli amene anachita mgwirizano ndi Aiguputo.
Mʼchilankhulo choyambirira, “Nebukadirezara.” Kameneka ndi kalembedwe kena ka dzinali.
Mawu a Chiheberi ali ndi tanthauzo lofanana ndi mawu akuti “ndowe” ndipo amagwiritsidwa ntchito posonyeza kuipidwa.
Kapena kuti, “Memfisi.”
Kapena kuti, “mtsogoleri.”
Amene ndi Thebesi.
Kapena kuti, “Memfisi.”
Amene ndi Heliyopolisi.
Kapena kuti, “Ndidzawonjezera mphamvu za mfumu.”
Mtengo wa junipa ndi wofanana ndi mtengo wa mkungudza.
Mʼchilankhulo choyambirira, “iwe.”
Kapena kuti, “kumanda.”
Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Kapena kuti, “kumanda.”
Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mʼchilankhulo choyambirira, “limodzi ndi dzanja lake.”
Kapena kuti, “udzatsitsidwira kumanda.”
Kapena kuti, “mkango waungʼono wamanyenje.”
Kapena kuti, “kumanda.”
Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Kapena kuti, “kumanda.”
Kapena kuti, “kumanda.”
Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Nʼkutheka kuti akunena za asilikali amene anaikidwa mʼmanda limodzi ndi malupanga awo, potsatira mwambo wachisilikali.
Kapena kuti, “kumanda.”
Kapena kuti, “atsogoleri.”
Kapena kuti, “kumanda.”
Kapena kuti, “koma ndidzafunsa mlondayo za magazi a munthuyo.”
Kapena kuti, “koma magazi ake ndidzawafuna kuchokera kwa iwe.”
Kapena kuti, “zopanda chilungamo.”
Kapena kuti, “nʼkumachita zopanda chilungamo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mumakweza maso anu nʼkuyangʼana.”
Mawu a Chiheberi ali ndi tanthauzo lofanana ndi mawu akuti “ndowe” ndipo amagwiritsidwa ntchito posonyeza kuipidwa.
Kapena kuti, “amalankhula mokopa.”
Kapena kuti, “asamawete.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “umene dzina lake lidzatchuka.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “aperekedwa kwa ife ngati chakudya.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “anthu amene anatsala.”
Mawu a Chiheberi ali ndi tanthauzo lofanana ndi mawu akuti “ndowe” ndipo amagwiritsidwa ntchito posonyeza kuipidwa.
Kutanthauza mtima wofuna kutsogoleredwa ndi Mulungu.
Mabaibulo ena amati, “ngati nkhosa zomwe ankapereka ngati nsembe ku Yerusalemu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Dzanja la Yehova linafika pa ine.”
Kapena kuti, “mpweya; mzimu.”
Kapena kuti, “mzimu.”
Kapena kuti, “amene ndi anzake.”
Kapena kuti, “amene ndi anzake.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Ana aamuna a anthu ako.”
Mawu a Chiheberi ali ndi tanthauzo lofanana ndi mawu akuti “ndowe” ndipo amagwiritsidwa ntchito posonyeza kuipidwa.
Mʼchilankhulo choyambirira, “ana awo aamuna.”
Kapena kuti, “kalonga.”
Kapena kuti, “Malo anga okhala adzakhala; Nyumba yanga.”
Kapena kuti, “idzawaphimba.”
Kapena kuti, “kalonga wamkulu.”
Kapena kuti, “kalonga wamkulu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mlonda.”
Kapena kuti, “mikango yamphamvu yamanyenje.”
Kapena kuti, “kalonga wamkulu.”
Mabaibulo ena amati, “zobayira.” Zimenezi ndi zida zokhala ndi nsonga zakuthwa.
Kapena kuti, “Chigwa cha Magulu a Anthu Amene Ankatsatira Gogi.”
Kutanthauza, “Magulu a Anthu Otsatira Gogi.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “dzanja limene.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Ndidzadzipereka kwambiri chifukwa cha dzina langa loyera.”
Kapena kuti, “pa tsiku dzanja la Yehova linali pa ine.”
Kapena kuti, “mkuwa.”
“Fulakesi” ndi mbewu imene ankalima ku Iguputo ndipo ankaigwiritsa ntchito popanga ulusi wowombera nsalu.
Onani Zakumapeto B14.
Mʼchilankhulo choyambirira, “mtima wako ukhale pa zonse.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “nyumba.” Mawu akuti “nyumba” agwiritsidwa ntchito mʼchaputala 40 mpaka 48 pamene akunena za malo onse pamene pali kachisi kapena ponena za kachisi weniweniyo.
Mkono umodzi ndi wofanana ndi masentimita 44 ndi hafu, ndipo “chikhatho” ndi chofanana ndi masentimita 7.4. Tikaphatikiza mkono ndi chikhatho ndi masentimita pafupifupi 51.8 ndipo zinkaimira muyezo umene unkadziwika kuti “mkono wautali.” Choncho bango loyezera la mikono 6 linali lalitali mamita 3.11. Onani Zakumapeto B14.
Nʼkutheka kuti akunena pamwamba pa khoma la chipinda cha alonda.
Kapena kuti, “ndinaona zipinda.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mulifupi.”
Mabaibulo ena amati, “12.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “kachisi.” Muchaputala 41 ndi 42, mawu amenewa akunena za kunja kwa malo opatulika (Malo Oyera) kapena malo opatulika onsewo (kachisi kuphatikiza Malo Oyera ndi Malo Oyera Koposa).
Imeneyi ndi mikono yaitali. Onani Zakumapeto B14.
Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼmbali mwa khomolo munali.”
Amenewa ndi Malo Oyera Koposa.
Mʼchilankhulo choyambirira, “mulifupi mwa khomo munali.”
Zikuoneka kuti kameneka kanali kanjira kozungulira kachisiyo.
Imeneyi ndi nyumba imene inali kumʼmawa kwa malo oyera.
Kapena kuti, “mkango wamphamvu wamanyenje.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Felemu lapakhomo la kachisi linali lofanana mbali zonse.” Nʼkutheka kuti akunena za khomo lolowera mʼMalo Oyera.
Nʼkutheka kuti akunena za Malo Oyera Koposa.
Mʼchilankhulo choyambirira, “mulitali mwake.”
Imeneyi ndi nyumba imene inali kumbuyo kwa kachisi.
Imeneyi ndi mikono yaitali. Onani Zakumapeto B14.
Kapena kuti, “zipindazo.”
Baibulo la Chigiriki la Septuagint limati: “Mikono 100 mulitali.” Malemba a Chiheberi amati: “Njira yokwana mkono umodzi.” Onani Zakumapeto B14.
Mʼchilankhulo choyambirira, “mulifupi.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Atamaliza kuyeza nyumba yamkati.”
Onani Zakumapeto B14.
Mabaibulo ena amati, “anapita.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼnyumba.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ayeze kamangidwe ka kachisiyu.”
Imeneyi ndi mikono yaitali. Onani Zakumapeto B14.
Umenewu ndi muyezo umene ukuchokera pansonga ya chala chamanthu cha dzanja lanu kukafika pansonga ya chala chachingʼono, mutatambasula zala. Muyezo umenewu ndi wokwana masentimita 22.2. Onani Zakumapeto B14.
Kapena kuti, “zopanda vuto lililonse.”
Kutanthauza kuti azidzaperekera anthuwo nsembe.
Mʼchilankhulo choyambirira, “mtima wako ukhale pa.”
Mawu a Chiheberi ali ndi tanthauzo lofanana ndi mawu akuti “ndowe” ndipo amagwiritsidwa ntchito posonyeza kuipidwa.
Kapena kuti, “mʼzipinda zopatulika.”
Imeneyi ndi mikono yaitali. Onani Zakumapeto B14.
Kapena kuti, “Malo onse amkati mwa malire ake.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mbali iyi 500, mbali inayo 500.”
Muyezo wa efa ndi wofanana ndi malita 22. Onani Zakumapeto B14.
Mtsuko umodzi unkakwana malita 22. Onani Zakumapeto B14.
Onani Zakumapeto B14.
Onani Zakumapeto B14.
Onani Zakumapeto B14.
Kapena kuti, “mina.” Onani Zakumapeto B14.
Onani Zakumapeto B14.
Onani Zakumapeto B14.
Onani Zakumapeto B14.
Onani Zakumapeto B14.
Kapena kuti, “lopita kuzipinda zopatulika.”
Imeneyi ndi mikono yaitali. Onani Zakumapeto B14.
Kapena kuti, “Onse 4 komanso tinyumba take tapakona tinali ndi muyezo wofanana.”
Imeneyi ndi mikono yaitali. Onani Zakumapeto B14.
Kapena kuti, “chigwa chamʼchipululu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mitsinje iwiriyo yapita.”
Imeneyi ndi nyanja ya Mediterranean.
Imeneyi ndi Nyanja Yakufa.
Kapena kuti, “kukafika polowera ku Hamati.”
Kapena kuti, “wopita polowera ku Hamati.”
Imeneyi ndi mikono yaitali. Onani Zakumapeto B14.
Imeneyi ndi nyanja ya Mediterranean.