YESAYA
1 Masomphenya amene Yesaya*+ mwana wa Amozi anaona, okhudza Yuda ndi Yerusalemu mʼmasiku a Uziya,+ Yotamu,+ Ahazi+ ndi Hezekiya,+ mafumu a Yuda:+
2 Imvani inu okhala kumwamba, ndipo tcherani khutu inu okhala padziko lapansi,+
Chifukwa Yehova wanena kuti:
3 Ngʼombe yamphongo imadziwa bwino munthu amene anaigula,
Ndipo bulu amadziwa chinthu chimene mbuye wake amamudyetseramo.
Anthu anga sachita zinthu mozindikira.”
Anthu olemedwa ndi zolakwa,
Ana a anthu ochita zoipa, ana a makhalidwe oipa.
5 Kodi mumenyedwanso pati mmene mukupitiriza kupandukamu?+
Mutu wanu uli ndi mabala okhaokha,
Ndipo mtima wanu ukudwala.+
6 Kuyambira kuphazi mpaka kumutu palibe pabwino.
Thupi lonse lili ndi mabala, zilonda, ndiponso lanyukanyuka.
Zilonda zanuzo sizinatsukidwe,* kumangidwa kapena kuthiridwa mafuta.+
7 Dziko lanu lawonongedwa.
Mizinda yanu yawotchedwa ndi moto.
Alendo akudya zokolola zochokera munthaka yanu, inu mukuona.+
Lawonongedwa ngati dziko limene lalandidwa ndi adani.+
8 Mwana wamkazi wa Ziyoni* wasiyidwa ngati msasa mʼmunda wa mpesa,
Ngati chisimba* mʼmunda wa nkhaka,
Ndiponso ngati mzinda umene wazunguliridwa ndi adani.+
9 Yehova wa magulu ankhondo akumwamba akanapanda kutisiyira anthu ochepa opulumuka,
Tikanakhala ngati Sodomu,
Ndipo tikanafanana ndi Gomora.+
10 Imvani mawu a Yehova, inu olamulira ankhanza a ku Sodomu.+
Mvetserani malamulo* a Mulungu wathu, inu anthu a ku Gomora.+
11 Yehova wanena kuti: “Kodi nsembe zanu zambirimbirizo zili ndi phindu lanji kwa ine?+
Nsembe zanu zopsereza za nkhosa zamphongo+ ndiponso mafuta a nyama zodyetsedwa bwino+ zandikwana.
Sindikusangalala ndi magazi+ a ngʼombe zazingʼono zamphongo,+ a ana a nkhosa ndiponso magazi a mbuzi.+
12 Inu mukabwera kudzaonekera pamaso panga,+
Kodi ndi ndani amene amakuuzani kuti muchite zimenezi,
Ndi ndani amene amakuuzani kuti muzipondaponda mabwalo a panyumba panga?+
13 Musabweretsenso nsembe zina za mbewu zomwe ndi zopanda phindu.
Zofukiza zanu ndi zonyansa kwa ine.+
Mumachita zikondwerero mwezi watsopano ukaoneka,+ mumasunga masabata,+ ndiponso mumaitanitsa misonkhano.+
Komanso ine ndatopa kukuonani mukugwiritsira ntchito mphamvu zamatsenga+ mukamachita msonkhano wanu wapadera.
14 Ndikudana ndi zikondwerero zimene mumachita mwezi watsopano ukaoneka komanso zikondwerero zina.
Zimenezi zasanduka katundu wolemera kwa ine,
Ndatopa ndi kuzinyamula.
17 Phunzirani kuchita zabwino, muzichita chilungamo,+
Dzudzulani munthu wopondereza ena,
Tetezani ufulu wa mwana wamasiye,
Ndipo muteteze mkazi wamasiye pa mlandu wake.”+
18 Yehova wanena kuti: “Bwerani tsopano, tiyeni tikambirane ndipo ine ndikuthandizani kuti mukhalenso pa ubwenzi wabwino ndi ine.+
Ngakhale kuti machimo anu ndi ofiira kwambiri,
Adzayera kwambiri.+
Ngakhale kuti ndi ofiira ngati magazi,
Adzayera ngati thonje.
20 Koma mukakana nʼkupanduka,
Mudzawonongedwa ndi lupanga,+
Chifukwa pakamwa pa Yehova mʼpamene panena zimenezi.”
21 Mzinda wokhulupirika+ uja wasanduka hule.+
Unali wodzaza ndi chilungamo+
Ndipo zachilungamo zinkakhala mwa iye,+
Koma tsopano muli zigawenga zopha anthu.+
23 Akalonga ako ndi osamva ndipo amagwirizana ndi anthu akuba.+
Aliyense wa iwo amakonda ziphuphu ndipo amalakalaka kupatsidwa mphatso.+
Mwana wamasiye samuweruza mwachilungamo,
Ndipo ngakhale mlandu wa mkazi wamasiye safuna kuuweruza.+
24 Choncho Ambuye woona, Yehova wa magulu ankhondo akumwamba,
Mulungu Wamphamvu wa Isiraeli, wanena kuti:
“Eya! Ndidzachotsa adani anga pamaso panga,
Ndipo ndidzabwezera adani anga.+
25 Ndidzakupatsani chilango,
Ndidzakuyengani nʼkuchotseratu zonyansa zanu zonse,
Ndidzachotsa zinthu zonse zimene zikuchititsa kuti musakhale oyera.+
Pambuyo pa zimenezi mudzatchedwa Mzinda Wachilungamo komanso Mzinda Wokhulupirika.+
27 Ziyoni adzawomboledwa ndi chilungamo+
Ndipo anthu ake amene adzabwerere, adzawomboledwanso ndi chilungamo.
29 Chifukwa iwo adzachita manyazi ndi mitengo ikuluikulu imene munkailakalaka,+
Ndipo mudzachititsidwa manyazi chifukwa cha minda imene munasankha.*+
30 Chifukwa mudzakhala ngati mtengo waukulu umene masamba ake akufota,+
Ndiponso ngati munda umene ulibe madzi.
31 Munthu wamphamvu adzakhala ngati udzu wouma,
Ndipo ntchito yake idzakhala ngati kamoto kakangʼono.
Zonsezi zidzayakira limodzi
Popanda wozizimitsa.”
2 Izi ndi zimene Yesaya mwana wa Amozi anaona zokhudza Yuda ndi Yerusalemu:+
2 Mʼmasiku otsiriza,
Phiri la nyumba ya Yehova
Lidzakhazikika pamwamba penipeni pa mapiri akuluakulu,+
Ndipo lidzakwezedwa kupitirira mapiri angʼonoangʼono.
Anthu a mitundu yonse adzapita kumeneko.+
3 Anthu ochokera mʼmitundu yosiyanasiyana adzabwera nʼkunena kuti:
“Bwerani. Tiyeni tipite kukakwera phiri la Yehova,
Tipite kunyumba ya Mulungu wa Yakobo.+
Iye akatiphunzitsa njira zake,
Ndipo ife tidzayenda mʼnjira zakezo.”+
Chifukwa chilamulo chidzaphunzitsidwa* mu Ziyoni,
Ndipo mawu a Yehova adzaphunzitsidwa mu Yerusalemu.+
4 Mulungu adzaweruza anthu a mitundu yosiyanasiyana
Ndipo adzakonza zinthu zimene ndi zolakwika pakati pawo.
Iwo adzasula malupanga awo kuti akhale makasu a pulawo,
Ndipo mikondo yawo adzaisula kuti ikhale zida zosadzira mitengo.+
Mtundu wa anthu sudzanyamula lupanga kuti umenyane ndi mtundu unzake,
Ndipo anthuwo sadzaphunziranso nkhondo.+
6 Inu mwasiya anthu anu, nyumba ya Yakobo,+
Chifukwa iwo ayamba kutsatira miyambo yambiri ya Kumʼmawa.
Akuchita zamatsenga+ ngati Afilisiti
Ndiponso ali ndi ana ambiri a alendo.
7 Dziko lawo ladzaza ndi siliva komanso golide,
Ndipo ali ndi chuma chopanda malire.
Dziko lawo ladzaza ndi mahatchi,
Ndipo ali ndi magaleta osawerengeka.+
8 Dziko lawo ladzaza ndi milungu yopanda phindu.+
Iwo amagwadira ntchito ya manja awo,
Amagwadira chinthu chimene zala zawo zapanga.
9 Choncho anthu agwada, anyozeka,
Ndipo simungawakhululukire.
10 Lowani muthanthwe ndipo mubisale mufumbi
Chifukwa cha kuopsa kwa mkwiyo wa Yehova,
Ndiponso chifukwa cha ulemerero wake waukulu.+
11 Maso odzikuza a munthu adzatsitsidwa,
Ndipo anthu odzikweza adzachititsidwa manyazi.
Yehova yekha ndi amene adzakwezedwe tsiku limenelo.
12 Chifukwa ndi tsiku la Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.+
Tsikulo lidzafikira aliyense wodzitukumula ndi wodzikweza,
Lidzafikira aliyense kaya ndi wolemekezeka kapena wonyozeka,+
13 Lidzafikira mikungudza yonse ya ku Lebanoni yomwe ndi yonyada komanso yodzikweza.
Lidzafikiranso mitengo ikuluikulu yonse ya ku Basana,
14 Lidzafikira mapiri onse akuluakulu odzikweza
Ndi mapiri onse angʼonoangʼono okwezeka,
15 Lidzafikiranso nsanja iliyonse yaitali ndi mpanda uliwonse wolimba kwambiri,
16 Lidzafikira sitima zonse zapamadzi za ku Tarisi+
Ndi ngalawa zonse zabwinozabwino.
17 Munthu wodzikuza adzatsitsidwa,
Ndipo anthu odzikweza adzachititsidwa manyazi.
Yehova yekha ndi amene adzakwezedwe tsiku limenelo.
18 Milungu yopanda phindu idzatheratu.+
19 Anthu adzalowa mʼmapanga a muthanthwe
Ndiponso mʼmayenje a munthaka,+
Chifukwa cha kuopsa kwa mkwiyo wa Yehova
Ndiponso chifukwa cha ulemerero wake waukulu+
Akaimirira kuti achititse dziko lapansi kunjenjemera ndi mantha.
20 Pa tsiku limenelo, anthu adzatenga milungu yawo yopanda pake yasiliva ndi yagolide,
Imene anaipanga kuti aziigwadira
Ndipo adzaitayira kumene kumakhala aswiswiri* ndi mileme,+
21 Kuti abisale mʼmayenje a mʼmatanthwe
Ndi mʼmingʼalu ya mʼmiyala ikuluikulu,
Chifukwa cha kuopsa kwa mkwiyo wa Yehova
Ndiponso chifukwa cha ulemerero wake waukulu
Akaimirira kuti achititse dziko lapansi kunjenjemera ndi mantha.
22 Kuti zinthu zikuyendereni bwino, siyani kudalira munthu wamba,
Amene ali ngati mpweya chabe wa mʼmphuno mwake.
Kodi pali chifukwa chilichonse choti munthu azimudalira?
3 Tamverani! Ambuye woona, Yehova wa magulu ankhondo akumwamba,
Akuchotsa mu Yerusalemu ndi mu Yuda zinthu zonse zofunika pa moyo,
Monga mkate ndi madzi.+
2 Akuchotsanso mwamuna wamphamvu, munthu wankhondo,
Woweruza, mneneri,+ woombeza, mkulu,
3 Mtsogoleri wa anthu 50,+ munthu wolemekezeka, mlangizi,
Katswiri wa matsenga komanso munthu waluso lodziwa kuseweretsa njoka.+
Mnyamata adzamenya munthu wachikulire,
Ndipo munthu wonyozeka adzalimbana ndi munthu wolemekezeka.+
6 Aliyense adzagwira mʼbale wake mʼnyumba mwa bambo ake nʼkumuuza kuti:
“Iwe uli ndi nsalu, ndiye ukhale wolamulira wathu.
Uzilamulira mulu wa bwinjawu.”
7 Tsiku limenelo iye adzakana nʼkunena kuti:
“Ine sindikufuna kukhala womanga* zilonda zanu.
Mʼnyumba mwanga mulibe chakudya kapena zovala.
Musandiike kuti ndikhale wolamulira anthuwa.”
9 Maonekedwe a nkhope zawo akuwachitira umboni wotsutsana nawo,
Ndipo anthuwo akunena za tchimo lawo mofanana ndi anthu a ku Sodomu.+
Iwo sanayese nʼkomwe kulibisa.
Tsoka kwa iwo, chifukwa akudzibweretsera mavuto.
10 Uzani anthu olungama kuti zidzawayendera bwino,
11 Tsoka kwa munthu woipa!
Iye adzakumana ndi mavuto aakulu,
Chifukwa zimene anachitira ena ndi manja ake, nayenso adzamuchitira zomwezo.
12 Amene amayangʼanira anthu anga akamagwira ntchito, akuwachitira nkhanza,
Ndipo akazi ndi amene akuwalamulira.
Inu anthu anga, atsogoleri anu akukusocheretsani,
Ndipo achititsa kuti musadziwe njira yoyenera kutsatira.+
13 Yehova wakhala pamalo ake kuti aimbe anthu mlandu,
Waimirira kuti aweruze mitundu ya anthu.
14 Yehova adzaweruza akulu komanso akalonga a anthu ake.
“Inuyo mwawotcha munda wa mpesa,
Ndipo zinthu zimene munaba kwa anthu osauka zili mʼnyumba zanu.+
15 Nʼchifukwa chiyani mukuphwanya anthu anga
Komanso kukhulitsa nkhope za anthu osauka padothi?”+ akutero Ambuye Wamkulu Koposa, Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.
16 Yehova wanena kuti: “Chifukwa chakuti ana aakazi a Ziyoni ndi onyada,
Akuyenda mwamatama,*
Amakopa amuna ndi maso awo, nʼkumayenda modzigomera,
Komanso amapanga phokoso chifukwa cha zodzikongoletsera zimene amavala mʼmiyendo yawo,
17 Yehova adzachititsa zipere mʼmutu mwa ana aakazi a Ziyoni,
Ndipo Yehova adzachititsa kuti mʼmutu mwawo mukhale mpala.+
18 Tsiku limenelo Yehova adzachotsa zodzikongoletsera zawo zonse.
Adzachotsa zibangili za mʼmiyendo, zinthu zomanga kumutu, zodzikongoletsera zooneka ngati mwezi,+
19 Ndolo, zibangili za mʼmanja, nsalu zofunda kumutu,
20 Maduku, matcheni ovala mʼmiyendo, malamba a pachifuwa,
Zoikamo mafuta onunkhira,* zithumwa,*
21 Mphete zovala mʼzala, mphete zovala pamphuno,
22 Mikanjo yovala pa nthawi zapadera, malaya ovala pamwamba, mikanjo yabwino kwambiri, tizikwama,
23 Magalasi amʼmanja odziyangʼanira,+ zovala,
Nduwira ndi nsalu zofunda kumutu.
24 Mʼmalo mwa mafuta onunkhira a basamu+ padzangokhala fungo loipa.
Mʼmalo mwa lamba padzakhala chingwe.
Mʼmalo mwa tsitsi lokonzedwa bwino padzakhala mpala.+
Mʼmalo mwa chovala chamtengo wapatali adzavala chiguduli,+
Ndipo padzakhala chipsera* mʼmalo mwa kukongola.
26 Malo olowera mumzinda adzalira ndipo adzamva chisoni,+
Mzindawo udzakhala padothi penipeni ndipo udzakhala wopanda chilichonse.”+
4 Tsiku limenelo, akazi 7 adzagwira mwamuna mmodzi+ nʼkumuuza kuti:
“Ife tizidya chakudya chathu
Ndipo tizidzipezera tokha zovala.
Inuyo mungotilola kuti tizitchedwa ndi dzina lanu
2 Tsiku limenelo, chinthu chimene Yehova adzachiphukitse chidzakhala chokongola komanso chaulemerero. Zipatso za mʼdzikolo zidzakhala zonyaditsa ndi zokongola kwa Aisiraeli amene adzapulumuke.+ 3 Aliyense amene adzatsale mu Ziyoni ndiponso amene adzasiyidwe mu Yerusalemu adzatchedwa woyera, anthu onse a mu Yerusalemu amene analembedwa mayina kuti akhale ndi moyo.+
4 Yehova akadzatsuka nyansi* za ana aakazi a Ziyoni+ ndiponso akadzatsuka magazi amene Yerusalemu anakhetsa, pogwiritsa ntchito mzimu wa chiweruzo komanso mzimu woyaka moto,+ 5 malo onse a paphiri la Ziyoni ndi malo onse a mu Yerusalemu ochitirapo misonkhano, Yehova adzawapangira mtambo ndi utsi kuti ziziwathandiza masana. Adzawapangiranso moto wowala walawilawi kuti uziwathandiza usiku,+ ndipo pamwamba pa malo onse aulemererowo padzakhala chotchinga. 6 Padzakhalanso msasa kuti uzipereka mthunzi woteteza ku dzuwa masana,+ ndiponso kuti ukhale malo othawirapo komanso achitetezo pa nthawi ya mphepo yamkuntho ndi mvula.+
5 Ndikufuna ndimuimbire nyimbo wokondedwa wanga
Nyimbo yonena za munthu amene ndimamukonda ndiponso munda wake wa mpesa.+
Wokondedwa wanga anali ndi munda wa mpesa pamalo achonde mʼmbali mwa phiri.
2 Iye analima mundawo nʼkuchotsamo miyala.
Anadzalamo mphesa zofiira zabwino kwambiri,
Anamanga nsanja pakati pa mundawo,
Komanso anasemamo choponderamo mphesa.+
Kenako ankayembekezera kuti mundawo ubereka mphesa zabwino,
Koma unangobereka mphesa zamʼtchire.+
3 “Tsopano inu anthu okhala mu Yerusalemu ndiponso inu amuna a mu Yuda,
Weruzani pakati pa ine ndi munda wanga wa mpesawu.+
Ine ndinkayembekezera kuti ubereka mphesa zabwino,
Koma nʼchifukwa chiyani unabereka mphesa zamʼtchire zokha?
5 Tsopano ndikuuzani
Zimene ndichite ndi munda wanga wa mpesawu:
Ndichotsa zomera zimene zinali ngati mpanda wa mundawo,
Ndipo uwotchedwa.+
Ndigumula mpanda wake wamiyala
Ndipo mundawo udzapondedwapondedwa.
Mʼmundamo mudzamera zitsamba zaminga komanso tchire,+
Ndipo ndidzalamula mitambo kuti isagwetse mvula pamundawo.+
7 Chifukwa nyumba ya Isiraeli ndi munda wa mpesa wa Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.+
Amuna a ku Yuda ndi mitengo ya mpesa imene ankaikonda kwambiri.
Iye ankayembekezera chilungamo,+
Koma pankachitika zinthu zopanda chilungamo.
Ankayembekezera zinthu zolungama
Koma ankangomva anthu akulira chifukwa chozunzidwa.”+
8 Tsoka kwa anthu amene akuwonjezera nyumba zina panyumba zawo,+
Ndiponso amene akuwonjezera minda ina kuminda yawo,+
Mpaka malo onse kutha,
Ndipo iwo ayamba kukhala okhaokha mʼdzikoli.
9 Yehova wa magulu ankhondo akumwamba walumbira ine ndikumva
Kuti nyumba zambiri, ngakhale kuti ndi zikuluzikulu komanso zokongola,
Zidzakhala chinthu chodabwitsa kwambiri
Ndipo simudzakhala aliyense.+
10 Chifukwa maekala 10* a munda wa mpesa adzatulutsa mtsuko* umodzi wokha wa vinyo,
Ndipo mbewu zokwana muyezo umodzi wa homeri* zidzatulutsa zokolola zokwana muyezo umodzi wokha wa efa.*+
11 Tsoka kwa anthu amene amadzuka mʼmamawa kwambiri kuti amwe mowa,+
Amene amakhala akumwabe mpaka madzulo kutada, moti vinyo amawaledzeretsa.
12 Pa zikondwerero zawo amaimbapo azeze, zoimbira za zingwe,
Maseche ndi zitoliro ndipo amamwapo vinyo.
Koma saganizira zochita za Yehova,
Ndipo saona ntchito ya manja ake.
13 Choncho anthu anga adzapita ku ukapolo kudziko lina
Chifukwa chosadziwa zinthu.+
Anthu awo olemekezeka adzakhala ndi njala,+
Ndipo anthu awo onse adzakhala ndi ludzu.
14 Choncho Manda* akulitsa malo ake
Ndipo atsegula kwambiri pakamwa pake kupitirira malire.+
Anthu olemekezeka a mumzindawo, khamu lake limene limachita phokoso komanso zikondwerero zake
Adzatsikira mʼmandamo.
16 Yehova wa magulu ankhondo akumwamba adzakwezeka chifukwa cha chiweruzo chake.*
Mulungu woona, Woyera,+ adzadziyeretsa kudzera mʼchilungamo.+
17 Kumeneko, ana a nkhosa amphongo adzadyako msipu ngati kuti ali pamalo odyetserapo ziweto.
Alendo adzadyera mʼmabwinja mmene kale munali nyama zodyetsedwa bwino.
18 Tsoka kwa amene amakoka zolakwa zawo ndi zingwe zachinyengo
Komanso amene amakoka machimo awo ndi zingwe zokokera ngolo.
19 Tsoka kwa amene amanena kuti: “Agwire ntchito yake mofulumira.
Ibwere mwamsanga kuti tiione.
20 Tsoka kwa amene akunena kuti chabwino nʼchoipa ndipo choipa nʼchabwino,+
Amene akuika mdima mʼmalo mwa kuwala ndi kuwala mʼmalo mwa mdima,
Amene akuika zowawa mʼmalo mwa zotsekemera ndi zotsekemera mʼmalo mwa zowawa.
22 Tsoka kwa anthu amene amatchuka ndi kumwa vinyo kwambiri,
Komanso kwa anthu amene ndi akatswiri odziwa kusakaniza mowa.+
23 Tsoka kwa anthu amene amaweruza kuti woipa alibe mlandu chifukwa choti alandira chiphuphu,+
Ndiponso kwa amene amalephera kuweruza anthu olungama mwachilungamo.+
24 Choncho, mofanana ndi mmene lawi la moto limapserezera mapesi
Komanso mmene udzu wouma umayakira mʼmalawi a moto,
Mizu yawo idzawola,
Ndipo maluwa awo adzauluzika ngati fumbi,
Chifukwa akana malamulo* a Yehova wa magulu ankhondo akumwamba
Ndipo anyoza mawu a Woyera wa Isiraeli.+
25 Nʼchifukwa chake mkwiyo wa Yehova wayakira anthu ake,
Ndipo adzatambasula dzanja lake nʼkuwalanga.+
Mapiri adzagwedezeka,
Ndipo mitembo yawo idzakhala ngati zinyalala mʼmisewu.+
Chifukwa cha zonsezi, mkwiyo wake sunabwerere,
Koma dzanja lake lidakali lotambasula kuti awalange.
26 Iye waikira chizindikiro mtundu wakutali.+
Wauimbira likhweru kuti ubwere kuchokera kumapeto kwa dziko lapansi.+
Ndipotu mtunduwo ukubwera mofulumira kwambiri.+
27 Pakati pawo palibe aliyense amene watopa kapena amene akupunthwa.
Palibe amene akuwodzera kapena amene akugona.
Lamba wa mʼchiuno mwawo sanamasulidwe,
Ndipo zingwe za nsapato zawo sizinaduke.
Ziboda za mahatchi awo nʼzolimba ngati mwala wa nsangalabwi,
Ndipo mawilo a magaleta awo ali ngati mphepo yamkuntho.+
Iwo adzabangula nʼkugwira nyama
Ndipo adzainyamula popanda woipulumutsa.
Munthu aliyense amene adzayangʼane dzikolo adzaona mdima wodetsa nkhawa.
Ngakhale kuwala kudzasanduka mdima chifukwa cha mitambo.+
6 Chaka chimene Mfumu Uziya inamwalira,+ ine ndinaona Yehova atakhala pampando wachifumu wolemekezeka komanso wokwezeka,+ ndipo zovala zake zinadzaza mʼkachisi. 2 Pamwamba pake panali aserafi. Mserafi aliyense anali ndi mapiko 6. Aliyense anaphimba nkhope yake ndi mapiko awiri, anaphimba mapazi ake ndi mapiko awiri ndipo mapiko ena awiriwo ankaulukira.
3 Aliyense ankauza mnzake kuti:
“Woyera, woyera, woyera ndi Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.+
Dziko lonse lapansi ladzaza ndi ulemerero wake.”
4 Chifukwa cha mawu ofuulawo, mafelemu a zitseko anayamba kunjenjemera ndipo mʼnyumbamo munadzaza utsi.+
5 Kenako ndinanena kuti: “Tsoka kwa ine!
Maso anga aona Mfumu, Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.
Ndifa ine basi,
Chifukwa ndine munthu wa milomo yodetsedwa,
Ndipo ndikukhala pakati pa anthu a milomo yodetsedwa.”+
6 Zitatero, mserafi mmodzi anaulukira kwa ine. Mʼmanja mwake munali khala lamoto+ limene analitenga paguwa lansembe ndi chopanira.+ 7 Iye anakhudza pakamwa panga nʼkunena kuti:
“Taona! Khalali lakhudza milomo yako.
Zolakwa zako zachotsedwa,
Ndipo tchimo lako laphimbidwa.”
8 Kenako ndinamva mawu a Yehova akufunsa kuti: “Kodi nditumize ndani, ndipo ndi ndani amene apite mʼmalo mwa ife?”+ Ine ndinayankha kuti: “Ine ndilipo! Nditumizeni.”+
9 Iye anamuuza kuti, “Pita ukauze anthu awa kuti:
‘Mudzamva mobwerezabwereza
Koma simudzamvetsetsa.
Mudzaona mobwerezabwereza,
Koma simudzazindikira chilichonse.’+
10 Uchititse anthu awa kuumitsa mtima wawo,+
Uchititse makutu awo kuti asamamve,+
Ndipo umate maso awo,
Kuti asamaone ndi maso awowo,
Ndiponso kuti asamamve ndi makutu awo,
Nʼcholinga choti mtima wawo usamvetse zinthu
Komanso kuti asabwerere nʼkuchiritsidwa.”
11 Atatero ndinafunsa kuti: “Mpaka liti, inu Yehova?” Iye anayankha kuti:
“Mpaka mizinda yawo itawonongedwa nʼkukhala mabwinja
Mpaka nyumba zawo zitakhala zopanda anthu okhalamo
Ndiponso mpaka dziko litawonongekeratu nʼkukhala bwinja.+
12 Mpaka Yehova atathamangitsira anthu kutali+
Ndiponso mpaka mbali yaikulu ya dzikolo itakhala bwinja.
13 Koma mʼdzikolo mudzakhalabe chakhumi ndipo chidzawotchedwanso ngati mtengo waukulu, ndiponso ngati chimtengo chachikulu, chimene chikadulidwa pamatsala chitsa. Mbewu* yopatulika idzakhala chitsa chake.”
7 Tsopano mʼmasiku a Ahazi+ mwana wa Yotamu mwana wa Uziya mfumu ya Yuda, Rezini mfumu ya Siriya ndi Peka+ mwana wa Remaliya mfumu ya Isiraeli, anapita kukamenyana ndi anthu amumzinda wa Yerusalemu koma analephera kulanda mzindawo.+ 2 Ndiyeno kunyumba ya Davide kunapita uthenga wakuti: “Dziko la Siriya lachita mgwirizano ndi dziko la Efuraimu.”
Choncho mtima wa Ahazi ndi wa anthu ake unayamba kunjenjemera, ngati mitengo ya mʼnkhalango imene ikugwedezeka ndi mphepo.
3 Kenako Yehova anauza Yesaya kuti: “Pita ukakumane ndi Ahazi. Upite ndi mwana wako Seari-yasubu.*+ Ukakumane naye kumapeto kwa ngalande yochokera kudziwe lakumtunda,+ mʼmphepete mwa msewu waukulu wopita kumalo a wochapa zovala. 4 Ukamuuze kuti, ‘Mtima wako ukhale mʼmalo. Usachite mantha ndipo usataye mtima chifukwa cha zitsa ziwirizi zimene zikungofuka utsi, chifukwa cha mkwiyo waukulu wa Rezini mfumu ya Siriya ndiponso mkwiyo wa mwana wa Remaliya.+ 5 Chifukwa Siriya ndi Efuraimu ndiponso mwana wa Remaliya akukonzera zoipa ndipo anena kuti: 6 “Tiyeni tikamenyane ndi dziko la Yuda ndipo tikalisakaze. Tikaligonjetse* nʼkulilanda ndipo tikaike mwana wa Tabeeli kuti akhale mfumu yake.”+
7 Koma Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti:
“Zimenezo sizitheka,
Ndipo sizichitika.
8 Chifukwa likulu la Siriya ndi Damasiko,
Ndipo mfumu ya Damasiko ndi Rezini.
Zaka 65 zisanathe,
Efuraimu adzakhala ataphwanyidwaphwanyidwa ndipo sadzakhalanso mtundu wa anthu.+
Mukapanda kukhala ndi chikhulupiriro cholimba,
Mukhala osatetezeka.”’”
10 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Ahazi kuti: 11 “Pempha chizindikiro kwa Yehova Mulungu wako.+ Chikhoza kukhala chozama ngati Manda* kapena chachitali ngati kumwamba.” 12 Koma Ahazi anati: “Sindipempha ndipo sindimuyesa Yehova.”
13 Kenako Yesaya ananena kuti: “Tamverani inu a mʼnyumba ya Davide. Kodi zimene mukuchita poyesa kuleza mtima kwa anthu nʼzosakwanira kwa inu? Kodi mukufunanso kuyesa kuleza mtima kwa Mulungu?+ 14 Choncho Yehova akupatsani chizindikiro: Tamverani! Mtsikana* adzakhala woyembekezera ndipo adzabereka mwana wamwamuna.+ Mwanayo adzamʼpatsa dzina lakuti Emanueli.*+ 15 Iye azidzadya bata* ndi uchi pamene azidzafika nthawi imene adzadziwe kukana choipa ndi kusankha chabwino. 16 Mwanayo asanafike podziwa kukana choipa ndi kusankha chabwino, mayiko a mafumu awiri amene ukuchita nawo manthawo, adzakhala atasiyidwiratu.+ 17 Yehova adzabweretsera iweyo, anthu ako komanso nyumba ya bambo ako nthawi yovuta imene sinakhaleponso kuyambira tsiku limene Efuraimu anapatukana ndi Yuda.+ Iye adzakubweretserani mfumu ya Asuri.+
18 Pa tsiku limenelo, Yehova adzaimbira likhweru ntchentche zimene zili mʼmitsinje ingʼonoingʼono yakutali yotuluka mumtsinje wa Nailo ku Iguputo komanso njuchi zimene zili mʼdziko la Asuri. 19 Ndipo zonse zidzabwera nʼkudzatera mʼzigwa zokhala* ndi maphompho, mʼmingʼalu ya mʼmatanthwe, pazitsamba zonse zaminga ndiponso mʼmalo onse omwetserapo ziweto.
20 Pa tsiku limenelo Yehova adzakumetani tsitsi la kumutu ndi tsitsi la mʼmiyendo pogwiritsira ntchito lezala lobwereka la kuchigawo cha ku Mtsinje,* pogwiritsira ntchito mfumu ya Asuri,+ ndipo lezalalo lidzametanso ndevu zanu.
21 Pa tsiku limenelo munthu adzasiya ngʼombe yaingʼono ndiponso nkhosa ziwiri zili zamoyo. 22 Chifukwa cha kuchuluka kwa mkaka, iye azidzadya bata, chifukwa bata ndi uchi nʼzimene munthu aliyense wotsala mʼdzikolo azidzadya.
23 Tsiku limenelo, pamalo alionse pamene panali mitengo ya mpesa 1,000, yokwana ndalama zasiliva 1,000, padzangokhala zitsamba zaminga ndi udzu. 24 Anthu azidzapita kumeneko atanyamula mivi ndi mauta, chifukwa mʼdziko lonselo mudzamera zitsamba zaminga ndi udzu. 25 Ndipo mʼmapiri onse amene anthu ankalambulako ndi makasu, sudzapitakonso chifukwa choopa zitsamba zaminga ndi udzu. Malowo adzakhala odyetserako ngʼombe zamphongo ndiponso oti nkhosa zizipondapondapo.”
8 Yehova anandiuza kuti: “Tenga cholembapo chachikulu+ ndipo ulembepo ndi cholembera wamba* kuti, ‘Maheri-salala-hasi-bazi.’* 2 Ndipo ndikufuna kuti mboni zokhulupirika zitsimikizire mochita kulemba.* Mbonizo zikhale wansembe Uriya+ ndi Zekariya mwana wa Yeberekiya.”
3 Kenako ndinagona ndi mneneri wamkazi* ndipo anakhala woyembekezera. Pambuyo pake anabereka mwana wamwamuna.+ Ndiyeno Yehova anandiuza kuti: “Umupatse dzina lakuti Maheri-salala-hasi-bazi, 4 chifukwa mwanayo asanadziwe kuitana kuti, ‘Ababa!’ kapena ‘Amama!’ chuma cha ku Damasiko ndi katundu wolandidwa ku Samariya zidzatengedwa nʼkupita nazo kwa mfumu ya Asuri.”+
5 Yehova anandiuzanso kuti:
6 “Popeza anthu awa akana madzi a ku Silowa*+ amene amayenda pangʼonopangʼono,
Ndipo akusangalala ndi Rezini ndiponso mwana wa Remaliya,+
7 Yehova adzawabweretsera
madzi ambiri komanso amphamvu a mu Mtsinje*
Omwe ndi mfumu ya Asuri+ ndi ulemerero wake wonse.
Mfumuyo idzadzaza timitsinje take tonse
Nʼkusefukira mʼmphepete mwake monse
8 Ndipo idzakokolola chilichonse mu Yuda.
Idzadutsa nʼkusefukira, moti idzafika mpaka mʼkhosi.+
Idzatambasula mapiko ake mpaka mʼlifupi mwa dziko lako,
9 Inu mitundu ya anthu, vulazani anthu, koma inuyo muphwanyidwaphwanyidwa.
Tamverani, inu nonse ochokera kumalekezero a dziko lapansi,
Konzekerani kumenya nkhondo, koma muphwanyidwaphwanyidwa.+
Konzekerani kumenya nkhondo, koma muphwanyidwaphwanyidwa.
10 Konzani pulani, koma idzalephereka.
11 Dzanja lamphamvu la Yehova linali pa ine, ndipo pofuna kundichenjeza kuti ndisayende panjira ya anthu awa, iye anati:
12 “Zimene anthu awa akumanena kuti ndi chiwembu, iwe usamanene kuti ndi chiwembu.
Usamaope zimene iwo amaopa,
Usamanjenjemere nazo.
13 Yehova wa magulu ankhondo akumwamba ndi amene uyenera kumuona kuti ndi woyera,+
Ndi amene uyenera kumuopa,
Ndipo ndi amene uyenera kumulemekeza.”+
14 Iye adzakhala ngati malo opatulika,
Koma kwa nyumba zonse ziwiri za Isiraeli,
Adzakhala ngati mwala wopunthwitsa+
Ndiponso ngati thanthwe lokhumudwitsa.
Adzakhala ngati msampha komanso khwekhwe
Kwa anthu okhala mu Yerusalemu.
15 Anthu ambiri pakati pawo adzapunthwa nʼkugwa ndipo adzathyoka.
Iwo adzakodwa nʼkugwidwa.
17 Ine ndipitiriza kuyembekezera* Yehova,+ amene wabisira nkhope yake nyumba ya Yakobo,+ ndithu ndiziyembekezera iyeyo.
18 Taonani, ine ndi ana amene Yehova wandipatsa+ tili ngati zizindikiro+ ndiponso ngati zodabwitsa mu Isiraeli, zochokera kwa Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, amene amakhala mʼphiri la Ziyoni.
19 Ndipo atakuuzani kuti: “Funsirani kwa anthu olankhula ndi mizimu kapena anthu olosera zamʼtsogolo, omwe amalira ngati mbalame ndiponso kulankhula motsitsa mawu,” kodi mungavomere? Kodi mtundu uliwonse wa anthu suyenera kufunsira kwa Mulungu wake? Kodi akuyenera kufunsira kwa anthu akufa pofuna kuthandiza anthu amoyo?+ 20 Mʼmalomwake, iwo azifufuza zimene chilamulo komanso maumboni olembedwa akunena!
Iwo akamalankhula zosemphana ndi mawu amenewa, ndiye kuti ali mumdima.*+ 21 Ndipo aliyense adzadutsa mʼdzikolo akuzunzika ndiponso ali ndi njala.+ Chifukwa chakuti ali ndi njala komanso wakwiya, adzatukwana mfumu yake ndi Mulungu wake ndipo azidzayangʼana kumwamba. 22 Kenako adzayangʼana padziko lapansi ndipo adzangoonapo kuzunzika, mdima, kusowa mtengo wogwira, nthawi zovuta, mdima wandiweyani ndipo sadzaonapo kuwala.
9 Komabe mdima wake sudzakhala ngati wa pa nthawi imene dzikolo linali mʼmavuto, ngati kale pamene anthu ankanyoza dziko la Zebuloni ndi dziko la Nafitali.+ Koma pakadzapita nthawi, Mulungu adzachititsa kuti anthu alemekeze dzikolo, dera limene kuli njira yamʼmphepete mwa nyanja, mʼchigawo cha Yorodano, ku Galileya kumene kunkakhala anthu a mitundu ina.
2 Anthu amene ankayenda mumdima
Aona kuwala kwakukulu.
Anthu amene ankakhala mʼdziko lamdima wandiweyani,
Kuwala kwawawalira.+
3 Mwapangitsa kuti mtundu ukhale waukulu.
Mwaupangitsa kuti usangalale kwambiri.
Iwo akusangalala pamaso panu
Ngati mmene anthu amasangalalira pa nthawi yokolola,
Ngati anthu amene amasangalala akamagawana katundu amene alanda.
4 Chifukwa mwathyolathyola goli la katundu wawo,
Ndodo yomwe inali pamapewa awo, ndodo ya amene ankawagwiritsa ntchito,
Ngati pa tsiku limene Amidiyani anagonjetsedwa.+
5 Nsapato iliyonse imene imagwedeza dziko lapansi munthu akamayenda
Ndi chovala chilichonse choviikidwa mʼmagazi
Zidzakhala zokolezera moto.
Iye adzapatsidwa dzina lakuti Mlangizi Wodabwitsa,+ Mulungu Wamphamvu,+ Atate Wamuyaya, Kalonga Wamtendere.
7 Ulamuliro* wake udzafika kutali
Ndipo mtendere sudzatha,+
Pampando wachifumu wa Davide+ ndiponso mu ufumu wake
Kuti iye achititse ufumuwo kukhazikika+ ndiponso kukhala wolimba
Pogwiritsa ntchito chilungamo+ ndiponso mtima wowongoka,+
Kuyambira panopa mpaka kalekale.
Yehova wa magulu ankhondo akumwamba adzachita zimenezi modzipereka kwambiri.
9 Anthu onse adzawadziwa,
Efuraimu ndi anthu okhala ku Samariya,
Amene chifukwa cha kudzikweza kwawo ndiponso mwano wamumtima mwawo amanena kuti:
Mitengo ya mkuyu yadulidwa,
Koma mʼmalo mwake ife tipezerapo mitengo ya mkungudza.”
11 Yehova adzakweza adani a Rezini kuti alimbane naye
Ndipo adzachititsa adani a Isiraeli kuti amuukire,
12 Siriya adzachokera kumʼmawa ndipo Afilisiti adzachokera kumadzulo,*+
Iwo adzadya Isiraeli ndi pakamwa potsegula.+
Chifukwa cha zonsezi, mkwiyo wake sunabwerere,
Koma dzanja lake lidakali lotambasula kuti awalange.+
13 Chifukwa anthuwo sanabwerere kwa Mulungu amene akuwamenya,
Ndipo sanafunefune Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.+
14 Choncho pa tsiku limodzi, Yehova adzadula Isiraeli
15 Munthu wachikulire komanso wolemekezeka kwambiri ndi amene ali mutu,
Ndipo mneneri wopereka malangizo abodza ndi amene ali mchira.+
16 Amene akutsogolera anthuwa ndi amene akuwasocheretsa,
Ndipo amene akutsogoleredwawo asokonezeka.
17 Nʼchifukwa chake Yehova sadzasangalala ndi anyamata awo,
Ndipo sadzamvera chisoni ana awo amasiye ndi akazi awo amasiye,
Chifukwa onsewo ndi ampatuko komanso ochita zoipa+
Ndipo pakamwa paliponse pakulankhula zopanda nzeru.
Chifukwa cha zonsezi, mkwiyo wake sunabwerere,
Koma dzanja lake lidakali lotambasula kuti awalange.+
18 Chifukwa kuipa kwayaka ngati moto,
Ndipo kukupsereza zitsamba zaminga ndi udzu.
Kuipako kudzayatsa zitsamba zowirira zamʼnkhalango,
Ndipo utsi wa mitengoyo udzakwera mʼmwamba kuti tolo!
19 Chifukwa cha mkwiyo wa Yehova wa magulu ankhondo akumwamba
Dzikolo lawotchedwa ndi moto,
Ndipo anthuwo adzakhala ngati nkhuni zokolezera motowo.
Palibe amene adzapulumutse ngakhale mʼbale wake.
20 Munthu adzacheka zimene zili kumbali yakumanja
Koma adzakhalabe ndi njala.
Ndipo munthu adzadya zimene zili kumanzere kwake
Koma sadzakhuta.
Awiriwa adzaukira Yuda limodzi.+
Chifukwa cha zonsezi, mkwiyo wake sunabwerere,
Koma dzanja lake lidakali lotambasula kuti awalange.+
10 Tsoka kwa amene akukhazikitsa malamulo oipa,+
Amene amangokhalira kulemba malamulo opondereza,
2 Kuti asamvetsere mlandu wa anthu osauka
Ndiponso kuti asachitire chilungamo anthu onyozeka amene ali pakati pa anthu anga.+
Amalanda katundu wa akazi amasiye
Komanso katundu wa ana amasiye.+
4 Palibe chimene mudzachite, koma mudzagwada pakati pa akaidi
Kapena mudzakhala mʼgulu la anthu ophedwa.
Chifukwa cha zonsezi, mkwiyo wake sunabwerere,
Koma dzanja lake lidakali lotambasula kuti awalange.+
5 Iye wanena kuti: “Eya! Onani Msuri,+
Iye ndi ndodo yosonyezera mkwiyo wanga+
Ndipo ndigwiritsa ntchito chikwapu chimene chili mʼdzanja lake popereka chilango.
6 Ndidzamutumiza kuti akalimbane ndi mtundu wopanduka,+
Kuti akalimbane ndi anthu amene andikwiyitsa.
Ndidzamulamula kuti akalande zinthu zambiri
Ndiponso kuti akapondeponde anthu ngati matope amumsewu.+
7 Koma iye sadzafuna kuchita zimenezi
Ndipo mtima wake sudzakonza zoti achite zimenezi.
Koma chifukwa chakuti mumtima mwake amaganiza zowononga,
Zoti awonongeretu mitundu yambiri, osati yochepa,
9 Kodi Kalino+ sali ngati Karikemisi?+
Kodi Hamati+ sali ngati Aripadi?+
Kodi Samariya+ sali ngati Damasiko?+
10 Dzanja langa lagwira maufumu olambira milungu yopanda phindu,
Amene zifaniziro zawo zogoba zinali zambiri kuposa za ku Yerusalemu ndi ku Samariya.+
11 Kodi zimene ndachitira Samariya ndi milungu yake yopanda phindu,+
Si zimenenso ndidzachitire Yerusalemu ndi mafano ake?’
12 Yehova akadzamaliza ntchito yake yonse mʼphiri la Ziyoni komanso mu Yerusalemu, adzalanga mfumu ya Asuri chifukwa cha mwano umene uli mumtima mwake ndiponso chifukwa chakuti amayangʼana monyada ndi modzikuza.+ 13 Chifukwa iye wanena kuti,
‘Ndidzachita zimenezi ndi mphamvu za manja anga
Ndiponso ndi nzeru zanga chifukwa ndine wanzeru.
Ndidzachotsa malire a mitundu ya anthu+
Ndipo ndidzatenga zinthu zawo zamtengo wapatali.+
Ngati munthu wamphamvu, ndidzagonjetsa anthu okhala mmenemo.+
14 Mofanana ndi munthu amene akupisa dzanja lake mʼchisa,
Dzanja langa lidzalanda zinthu zofunika za anthu a mitundu ina.
Ngati mmene munthu amasonkhanitsira mazira amene asiyidwa,
Ine ndidzasonkhanitsa zinthu zonse zapadziko lapansi.
Palibe aliyense amene adzakupize mapiko ake kapena kutsegula pakamwa pake kapenanso kulira ngati mbalame.’”
15 Kodi nkhwangwa ingadzikuze pamaso pa munthu amene akuigwiritsa ntchito?
Kodi chochekera matabwa chingadzikweze pamaso pa munthu amene akuchigwiritsa ntchito?
Kodi chikwapu+ chinganyamule munthu amene wachinyamula mʼmwamba,
Kapena kodi ndodo inganyamule mʼmwamba munthu amene si mtengo?
16 Choncho Ambuye woona, Yehova wa magulu ankhondo akumwamba
Adzachititsa kuti anthu ake* onenepa awonde,+
Ndipo pansi pa ulemerero wake adzayatsapo moto.+
17 Kuwala kwa Isiraeli+ kudzasanduka moto+
Ndipo Woyera wake adzasanduka lawi lamoto.
Motowo udzayaka nʼkupsereza udzu wake komanso zitsamba zake zaminga pa tsiku limodzi.
18 Mulungu adzathetseratu ulemerero wa nkhalango yake ndi wa munda wake wa zipatso,
Ndipo zidzakhala ngati munthu wodwala amene akuonda.+
19 Mitengo yotsala yamʼnkhalango mwake
Idzakhala yochepa kwambiri moti kamnyamata kadzatha kulemba chiwerengero chake.
20 Tsiku limenelo, otsala a Isiraeli
Ndi amʼnyumba ya Yakobo amene adzapulumuke
Sadzadaliranso amene anawamenya,+
Koma ndi mtima wonse adzadalira Yehova,
Woyera wa Isiraeli.
22 Ngakhale kuti anthu ako iwe Isiraeli,
Ali ngati mchenga wakunyanja,
Otsala ochepa okha pakati pawo ndi amene adzabwerere.+
Mulungu wakonza zoti anthuwo awonongedwe+
Ndipo chilango cholungama chidzawabwerera ngati madzi osefukira.+
23 Zimene Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Ambuye Wamkulu Koposa, wakonza zoti awononge anthuwo,
Zidzachitika padziko lonselo.+
24 Choncho Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Anthu anga amene mukukhala mʼZiyoni, musachite mantha chifukwa cha Msuri amene ankakukwapulani ndi chikwapu+ ndiponso kukumenyani ndi ndodo, ngati mmene ankachitira Iguputo.+ 25 Chifukwa pakangodutsa kanthawi kochepa, kudzudzulako kudzatha ndipo mkwiyo wanga udzawayakira, moti adzawonongedwa.+ 26 Yehova wa magulu ankhondo akumwamba adzamʼkwapula ndi chikwapu+ ngati mmene anachitira pamene anagonjetsa Midiyani pathanthwe la Orebi.+ Adzatambasula ndodo yake ndi kuloza panyanja ndipo adzaikweza mʼmwamba ngati mmene anachitira ndi Iguputo.+
27 Tsiku limenelo katundu wake adzachoka paphewa panu,+
Ndipo goli lake lidzachoka mʼkhosi mwanu.+
Golilo lidzathyoledwa+ chifukwa cha mafuta.”
30 Iwe mwana wamkazi wa Galimu, lira ndi kufuula kwambiri.
Khala tcheru iwe Laisa,
Iwenso Anatoti womvetsa chisoni!+
31 Madimena wathawa.
Anthu okhala ku Gebimu abisala.
32 Tsiku lomwelo iye akaima ku Nobu.+
Iye akuopseza ndi chibakera phiri la mwana wamkazi wa Ziyoni,*
Phiri limene pali Yerusalemu.
33 Taonani! Ambuye woona, Yehova wa magulu ankhondo akumwamba,
Akudula nthambi ndipo zikugwa ndi mkokomo waukulu.+
Mitengo italiitali ikudulidwa,
Ndipo imene ili mʼmwamba ikutsitsidwa.
34 Iye wadula ndi nkhwangwa zitsamba zowirira zamʼnkhalango,
Ndipo wamphamvu adzawononga Lebanoni.
2 Mzimu wa Yehova udzakhazikika pa iye,+
Mzimu wanzeru+ ndi womvetsa zinthu,
Mzimu wopereka malangizo abwino ndi wamphamvu,+
Mzimu wodziwa zinthu ndi woopa Yehova.
3 Iye adzasangalala ndi kuopa Yehova.+
Sadzaweruza potengera zimene wangoona ndi maso ake,
Kapena kudzudzula potengera zimene wangomva ndi makutu ake.+
4 Adzaweruza mwachilungamo anthu onyozeka,
Ndipo adzadzudzula anthu mowongoka mtima, pothandiza ofatsa apadziko lapansi.
Adzakwapula dziko lapansi ndi ndodo ya pakamwa pake+
Ndipo adzapha anthu oipa pogwiritsa ntchito mpweya* wamʼkamwa mwake.+
6 Mmbulu udzakhala pamodzi ndi mwana wa nkhosa kwa kanthawi,+
Ndipo kambuku adzagona pansi ndi mbuzi yaingʼono,
Mwana wa ngʼombe, mkango wamphamvu ndi nyama yonenepa zidzakhala pamodzi,*+
Ndipo kamnyamata kakangʼono kadzazitsogolera.
7 Ngʼombe ndi chimbalangondo zidzadyera pamodzi
Ndipo ana awo adzagona pansi pamodzi.
Mkango udzadya udzu ngati ngʼombe yamphongo.+
8 Mwana woyamwa adzasewera pa una wa mamba,
Ndipo mwana amene anasiya kuyamwa adzapisa dzanja lake kudzenje la njoka yapoizoni.
Kapena kuwonongana mʼphiri langa lonse loyera,+
Chifukwa dziko lapansi lidzadzaza ndi anthu odziwa Yehova
Ngati mmene madzi amadzazira mʼnyanja.+
10 Pa tsiku limenelo muzu wa Jese+ udzaimirira ngati chizindikiro kwa anthu.+
Anthu a mitundu ina adzatembenukira kwa iye kuti awapatse malangizo,*+
Ndipo malo ake okhalapo adzakhala aulemerero.
11 Pa tsiku limenelo Yehova adzaperekanso dzanja lake kachiwiri kuti atenge anthu ake otsala kuchokera ku Asuri,+ ku Iguputo,+ ku Patirosi,+ ku Kusi,+ ku Elamu,+ ku Sinara,* ku Hamati ndi mʼzilumba zamʼnyanja.+ 12 Iye adzakwezera chizindikiro mitundu ya anthu nʼkusonkhanitsa Aisiraeli omwe anamwazikana.+ Ndipo adzasonkhanitsa pamodzi Ayuda omwe anabalalika, kuchokera kumakona 4 a dziko lapansi.+
Efuraimu sadzachitira nsanje Yuda,
Ndiponso Yuda sadzadana ndi Efuraimu.+
14 Iwo adzatsika zitunda za* Afilisiti kumadzulo.
Onsewa pamodzi, adzalanda katundu wa anthu a Kumʼmawa.
Pogwiritsa ntchito mpweya* wake wotentha, adzamenya timitsinje 7 tamtsinjewo,*
Ndipo adzachititsa anthu kuwoloka atavala nsapato zawo.
16 Padzakhala msewu waukulu+ wochokera kudziko la Asuri woti mudzadutse anthu ake amene adzatsale,+
Ngati mmene zinalili kwa Aisiraeli pamene ankatuluka mʼdziko la Iguputo.
12 Pa tsiku limenelo ndithu udzanena kuti:
“Ndikukuthokozani, inu Yehova
Chifukwa ngakhale munandikwiyira,
Mkwiyo wanu unachepa pangʼonopangʼono ndipo munanditonthoza.+
2 Taonani! Mulungu ndi chipulumutso changa.+
Ndidzamukhulupirira ndipo sindidzaopa chilichonse,+
Chifukwa Ya,* Yehova, ndi mphamvu zanga komanso nyonga zanga,
Ndipo iye wakhala chipulumutso changa.”+
4 Pa tsiku limenelo mudzanena kuti:
“Yamikani Yehova, itanani pa dzina lake,
Dziwitsani mitundu ya anthu ntchito zake.+
Lengezani kuti dzina lake ndi lokwezeka.+
5 Imbani nyimbo zotamanda Yehova,+ chifukwa wachita zinthu zodabwitsa.+
Lengezani zimenezi padziko lonse lapansi.
6 Fuulani mwachisangalalo inu okhala mu Ziyoni,*
Chifukwa Woyera wa Isiraeli amene ali pakati panu ndi wamkulu.”
13 Uwu ndi uthenga wokhudza Babulo,+ umene Yesaya+ mwana wa Amozi anaona mʼmasomphenya:
2 “Imikani chizindikiro+ paphiri la miyala yokhayokha.
Afuulireni! Akodoleni ndi dzanja lanu,
Kuti adzalowe pamakomo a anthu olemekezeka.
3 Ine ndapereka lamulo kwa anthu amene ndawasankha.*+
Ndaitana asilikali anga kuti adzasonyeze mkwiyo wanga.
Iwo amasangalala komanso kunyada.
4 Tamverani! Mʼmapiri mukumveka phokoso la gulu la anthu.
Phokosolo likumveka ngati la anthu ambiri,
Tamverani! Kukumveka phokoso losonyeza kuti maufumu asokonezeka,
Phokoso la mitundu ya anthu imene yasonkhanitsidwa pamodzi.+
Yehova wa magulu ankhondo akumwamba akusonkhanitsira asilikali kunkhondo.+
5 Iwo akubwera kuchokera kudziko lakutali,+
Kuchokera kumalo akutali kwambiri pansi pa thambo,
Yehova akubwera ndi zida zamkwiyo wake,
Kuti awononge dziko lonse lapansi.+
6 Lirani mofuula, chifukwa tsiku la Yehova lili pafupi.
Lidzabwera ngati chiwonongeko chochokera kwa Wamphamvuyonse.+
7 Nʼchifukwa chake manja onse adzangoti lobodo,
Ndipo mtima wa munthu aliyense udzasungunuka ndi mantha.+
Nsautso ndi zowawa zawagwera
Ngati mkazi amene akubereka.
Akuyangʼanana mwamantha,
Ndipo nkhope zawo zikuonekeratu kuti ali ndi nkhawa.
9 Taonani! Tsiku la Yehova likubwera,
Tsikulo ndi lankhanza, laukali ndiponso lamkwiyo woyaka moto,
Likubwera kuti lidzachititse dziko kukhala chinthu chochititsa mantha,+
Ndiponso kuti lidzawononge anthu ochimwa amʼdzikolo.
10 Chifukwa nyenyezi zakumwamba ndi magulu awo*+
Sizidzaonetsa kuwala kwawo.
Dzuwa lidzachita mdima potuluka,
Ndipo mwezi sudzaonetsa kuwala kwake.
11 Ndidzaimba mlandu anthu okhala padziko lapansi chifukwa cha zoipa zawo,+
Ndiponso anthu oipa chifukwa cha zolakwa zawo.
Ndidzathetsa kunyada kwa anthu odzikuza
Ndidzatsitsa kudzikuza kwa olamulira ankhanza.+
12 Ndidzachititsa kuti anthu azisowa kwambiri kuposa golide woyengedwa bwino,+
Ndiponso ndidzachititsa kuti anthu azisowa kwambiri kuposa golide wa ku Ofiri.+
13 Choncho ndidzachititsa kuti kumwamba kunjenjemere,
Ndipo dziko lapansi lidzagwedezeka nʼkuchoka mʼmalo mwake+
Chifukwa cha ukali wa Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, pa tsiku limene mkwiyo wake udzayake.
14 Mofanana ndi insa imene ikuthamangitsidwa ndiponso mofanana ndi ziweto zimene zilibe wozisonkhanitsa pamodzi,
Aliyense adzabwerera kwa anthu ake.
Aliyense adzathawira kudziko lake.+
16 Ana awo adzaphwanyidwaphwanyidwa iwo akuona,+
Katundu wamʼnyumba zawo adzalandidwa,
Ndipo akazi awo adzagwiriridwa.
18 Mauta awo adzaphwanyaphwanya anyamata.+
Iwo sadzamvera chisoni chipatso cha mimba
Kapena kuchitira chifundo ana.
19 Babulo, amene ndi waulemerero kwambiri* kuposa maufumu onse,+
Chinthu chokongola chimene Akasidi amachinyadira,+
Adzakhala ngati Sodomu ndi Gomora pa nthawi imene Mulungu anawononga mizindayi.+
Kumeneko Mluya sadzakhomako tenti yake
Ndipo abusa sadzagonekako ziweto zawo.
21 Nyama zamʼchipululu zidzagona kumeneko.
Nyumba zawo zidzadzaza ndi akadzidzi.
22 Nyama zakutchire zizidzalira munsanja zake,
Ndipo mimbulu izidzalira mʼnyumba zake zachifumu zokongola.
Nthawi yoti apatsidwe chilango yayandikira, ndipo zimenezi zichitika posachedwa.”+
14 Yehova adzachitira chifundo Yakobo+ ndipo adzasankhanso Isiraeli.+ Iye adzachititsa kuti akhazikike* mʼdziko lawo,+ alendo adzagwirizana nawo ndipo adzakhala limodzi ndi nyumba ya Yakobo.+ 2 Anthu a mitundu ina adzawatenga nʼkubwerera nawo kwawo ndipo nyumba ya Isiraeli idzatenga anthuwo kuti akhale antchito awo aamuna ndi aakazi+ mʼdziko la Yehova. Iwo adzagwira anthu amene anawagwira nʼkupita nawo kudziko lina ndipo azidzalamulira anthu amene ankawagwiritsa ntchito mokakamiza.
3 Tsiku limene Yehova adzakupatseni mpumulo ku ululu wanu nʼkuthetsa chipwirikiti komanso ukapolo wanu wowawa,+ 4 mudzanena mwambi uwu wonyoza mfumu ya Babulo:
“Amene ankagwiritsa ntchito anzake mokakamiza uja wawonongedwa!
Kuponderezedwa kuja kwatha ndithu!+
5 Yehova wathyola ndodo ya anthu oipa,
Ndodo ya anthu olamulira.+
6 Wathyola ndodo ya amene ankakwapula mwaukali komanso mosalekeza anthu a mitundu ina,+
Amene anagonjetsa mitundu ya anthu mokwiya powazunza mosalekeza.+
7 Tsopano dziko lonse lapansi lapuma, palibenso chosokoneza.
Anthu akufuula mosangalala.+
8 Ngakhale mitengo ya junipa* yasangalala ndi zimene zakuchitikira,
Limodzi ndi mitengo ya mkungudza ya ku Lebanoni.
Mitengoyi ikunena kuti, ‘Kuyambira pamene unaphedwa,
Palibenso munthu wodula mitengo amene anabwera kudzatidula.’
Chifukwa cha iwe, Mandawo adzutsa akufa,
Adzutsa atsogoleri* onse opondereza apadziko lapansi.
Amachititsa mafumu onse a mitundu ya anthu kunyamuka pamipando yawo yachifumu.
10 Onsewo akulankhula nawe kuti,
‘Kodi iwenso wafooka ngati ife?
Kodi wafanana ndi ife?
Mphutsi zayalana pansi pako ngati bedi,
Ndipo nyongolotsi zasanduka chofunda chako.’
12 Wagwa kuchokera kumwamba,
Wonyezimirawe, iwe mwana wa mʼbandakucha!
Wadulidwa nʼkugwera padziko lapansi,
Iwe amene unagonjetsa mitundu ya anthu!+
13 Iweyo wanena mumtima mwako kuti, ‘Ndikwera kumwamba.+
Ndikweza mpando wanga wachifumu pamwamba pa nyenyezi za Mulungu,+
Ndipo ndikhala paphiri lokumanapo
Kumapeto kwenikweni kwa madera akumpoto.+
14 Ndikwera pamwamba kupitirira nsonga za mitambo.
Ndidzipanga kukhala wofanana ndi Wamʼmwambamwamba.’
16 Okuona adzakuyangʼana modabwa.
Adzakuyangʼanitsitsa nʼkunena kuti,
‘Kodi munthu amene ankagwedeza dziko lapansi uja ndi ameneyu,
Amene ankachititsa kuti maufumu anjenjemere,+
17 Amene anachititsa dziko lapansi kukhala ngati chipululu,
Nʼkugonjetsa mizinda yake,+
Amene sanalole kuti akaidi ake azipita kwawo?’+
19 Koma iweyo watayidwa popanda kuikidwa mʼmanda,
Ngati mphukira* imene anthu amanyansidwa nayo,
Imene ili pakati pa anthu akufa ophedwa ndi lupanga,
Amene amatsikira kumiyala yamʼdzenje,
Ngati mtembo wopondedwapondedwa.
20 Sudzaikidwa mʼmanda limodzi ndi mafumuwo,
Chifukwa unawononga dziko lako lomwe,
Unapha anthu ako omwe.
Mayina a ana a anthu ochita zoipa sadzatchulidwanso.
21 Konzekerani kupha ana ake
Chifukwa cha zolakwa za makolo awo,
Kuti asakhalenso ndi mphamvu nʼkuyamba kulamulira dziko lapansi
Komanso kudzaza dzikoli ndi mizinda yawo.”
22 “Ine ndidzawaukira,”+ akutero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.
“Ndipo mʼBabulo ndidzachotsamo dzina, anthu otsala, ana komanso mbadwa,”+ akutero Yehova.
23 “Babulo ndidzamusandutsa malo okhala nungu* ndiponso malo a zithaphwi. Ndidzamusesa ndi tsache la chiwonongeko,”+ akutero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.
24 Yehova wa magulu ankhondo akumwamba walumbira kuti:
“Zimene ndikufuna kuchita, zidzachitika mmene ndikufunira,
Ndipo zimene ndasankha, ndi zimene zidzachitike.
Goli lake lidzachotsedwa pa iwo
Ndipo katundu wake adzachotsedwa pamapewa awo.”+
26 Izi nʼzimene zakonzedwa kuti zidzachitikire dziko lonse lapansi,
Ndipo ili ndi dzanja limene latambasulidwa* kuti lilange mitundu yonse ya anthu.
27 Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wasankha zoti achite,
Ndiye ndi ndani amene angazilepheretse?+
Dzanja lake latambasulidwa,
Ndi ndani amene angalibweze?+
28 Mʼchaka chimene Mfumu Ahazi inamwalira,+ uthenga wamphamvu uwu unaperekedwa:
29 “Usasangalale iwe Filisitiya, kapena aliyense wokhala mwa iwe
Chifukwa chakuti ndodo ya amene ankakumenya yathyoka.
Chifukwa pamuzu wa njoka+ padzatuluka njoka yapoizoni,+
Ndipo mwana wake adzakhala njoka youluka, yaululu wamoto.*
30 Ana oyamba kubadwa a anthu onyozeka adzadya nʼkukhuta
Ndipo anthu osauka adzagona motetezeka,
Koma ndidzapha anthu ako* ndi njala,
Ndipo amene adzatsale mwa iwe adzaphedwa.+
31 Lira mofuula geti iwe! Lira mokweza mzinda iwe!
Nonsenu mudzataya mtima, inu anthu a ku Filisitiya!
Chifukwa utsi ukubwera kuchokera kumpoto,
Ndipo palibe msilikali amene akutsalira pa magulu ake ankhondo.”
32 Kodi iwo adzawayankha chiyani amithenga ochokera ku mtundu wina?
Adzawayankha kuti, Yehova waika maziko a Ziyoni,+
Ndipo anthu onyozeka pakati pa anthu ake adzathawira mmenemo.
15 Uwu ndi uthenga wokhudza Mowabu:+
Chifukwa chakuti wawonongedwa usiku umodzi wokha,
Ari+ wa ku Mowabu wakhalitsidwa chete.
Chifukwa chakuti wawonongedwa usiku umodzi wokha,
Kiri+ wa ku Mowabu wakhalitsidwa chete.
Mowabu akulira mofuula chifukwa cha zimene zachitikira Nebo+ ndi Medeba.+
Mutu uliwonse aumeta mpala+ ndipo ndevu zonse zametedwa.+
3 Anthu avala ziguduli mʼmisewu yake.
Pamadenga awo komanso mʼmabwalo a mizinda yawo, onse akulira mofuula.
Akulira nʼkumapita kumunsi.+
Nʼchifukwa chake amuna onyamula zida a ku Mowabu akungofuula.
Iwo akunjenjemera kwambiri.
5 Mtima wanga ukulirira Mowabu.
Anthu ake athawira kutali, ku Zowari+ ndi ku Egilati-selisiya.+
Iwo akulira pamene akukwera mtunda wa Luhiti.
Panjira yopita ku Horonaimu, iwo akulira kwambiri chifukwa cha tsokalo.+
6 Madzi a ku Nimurimu aumiratu.
Msipu wobiriwira wauma,
Udzu watha ndipo palibenso chilichonse chobiriwira chimene chatsala.
7 Nʼchifukwa chake akunyamula zinthu zimene zatsala pa katundu amene anasunga komanso chuma chawo.
Iwo akuwoloka chigwa* cha mitengo ya msondodzi.
8 Chifukwa kulira kwake kwamveka mʼdziko lonse la Mowabu.+
Kulira kwake kofuula kwamveka mpaka ku Egilaimu.
Kulira kwake kofuula kwamveka mpaka ku Beere-elimu.
9 Madzi onse a ku Dimoni adzaza magazi,
Ndipo Mulungu adzamʼbweretsera Dimoni masoka ambiri,
Adzatumiza mikango kwa anthu a ku Mowabu amene adzathawe
Komanso kwa anthu otsala mʼdzikolo.+
16 Tumizani nkhosa yamphongo kwa wolamulira wa dziko,
Kuchokera ku Sela kudutsa kuchipululu
Kukafika kuphiri la mwana wamkazi wa Ziyoni.*
2 Pamalo owolokera chigwa cha Arinoni,+
Ana aakazi a Mowabu adzakhala ngati mbalame yomwe yathamangitsidwa pachisa chake.+
3 “Perekani malangizo, chitani zimene zagamulidwa.
Chititsani kuti masana, mthunzi wanu ukhale waukulu ndipo uchititse mdima ngati wa usiku.
Bisani anthu amene abalalitsidwa ndipo amene akuthawa musawapereke kwa adani awo.
4 Anthu anga amene abalalitsidwa akhale mʼdziko lako, iwe Mowabu.
Iwe ukhale malo awo obisalamo pamene akuthawa wowononga.+
Wopondereza adzafika pamapeto ake,
Chiwonongeko chidzatha,
Ndipo amene akupondaponda anzawo adzatha padziko lapansi.
5 Kenako mpando wachifumu udzakhazikika chifukwa cha chikondi chokhulupirika.
Amene adzakhale pampandowo mutenti ya Davide adzakhala wokhulupirika.+
Iye adzaweruza mwachilungamo, ndipo adzachita mwachangu zinthu zachilungamo.”+
6 Ife tamva za kunyada kwa Mowabu, iye ndi wonyada kwambiri.+
Tamva za kudzikweza kwake, kunyada kwake ndi mkwiyo wake.+
Koma zolankhula zake zopanda pake sizidzachitika.
7 Choncho Mowabu adzalira mofuula chifukwa cha tsoka lake.
Aliyense wokhala mʼMowabu adzalira mofuula.+
Omenyedwawo adzalirira mphesa zouma zoumba pamodzi za ku Kiri-hareseti.+
8 Chifukwa minda yamʼmapiri ya ku Hesiboni+ yafota,
Chimodzimodzinso mitengo ya mpesa ya ku Sibima,+
Olamulira anthu a mitundu ina apondaponda nthambi zake zofiira kwambiri.*
Nthambizo zinafika mpaka ku Yazeri,+
Zinafika mpaka kuchipululu.
Mphukira zake zinakula mpaka zinafika kunyanja.
9 Nʼchifukwa chake ndidzalirire mtengo wa mpesa wa ku Sibima pamene ndikulirira Yazeri.
Ndidzakunyowetsa kwambiri ndi misozi yanga iwe Hesiboni ndi Eleyale,+
Chifukwa chakuti kufuula kosangalalira zipatso zamʼchilimwe komanso zokolola zako kwatha.*
10 Kukondwera ndi kusangalala zachotsedwa mʼmunda wako wazipatso,
Ndipo mʼminda ya mpesa simukumveka nyimbo zachisangalalo kapena kufuula.+
Oponda mphesa sakupondanso mphesa kuti apange vinyo,
Chifukwa ndachititsa kuti kufuula kulekeke.+
11 Nʼchifukwa chake mkati mwanga mukunjenjemera chifukwa cha Mowabu,+
Mukunjenjemera ngati zingwe za zeze,
Ndipo mʼmimba mwanga mukunjenjemera chifukwa cha Kiri-hareseti.+
12 Ngakhale Mowabu atadzitopetsa pamalo okwezeka nʼkupita kukapemphera kumalo ake opatulika, sadzapindula chilichonse.+
13 Awa ndi mawu okhudza Mowabu amene Yehova ananena mʼmbuyomu. 14 Koma tsopano Yehova wanena kuti: “Pomatha zaka zitatu, mofanana ndi zaka za munthu waganyu,* ulemerero wa Mowabu udzatha. Iye adzachititsidwa manyazi ndipo adzakumana ndi chipwirikiti chamtundu uliwonse ndipo anthu amene adzatsale adzakhala ochepa kwambiri ndiponso opanda mphamvu.”+
17 Uwu ndi uthenga wokhudza Damasiko:+
“Taonani! Damasiko sadzakhalanso mzinda,
Adzawonongedwa nʼkukhala mabwinja okhaokha.+
2 Mizinda ya Aroweri+ idzasiyidwa.
Idzasanduka malo amene ziweto zimagona
Popanda aliyense woziopseza.
3 Mu Efuraimu simudzakhalanso mizinda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri+
Ndipo mu Damasiko simudzakhalanso ufumu.+
Anthu amene adzatsale mu Siriya
Adzakhala ngati ulemerero wa Aisiraeli,”* akutero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.
4 “Pa tsiku limenelo, ulemerero wa Yakobo udzachepa,
Ndipo thupi lake lonenepa lidzaonda.
5 Zidzakhala ngati zimene zimachitika wokolola akamadula tirigu mʼmunda
Komanso dzanja lake likamakolola ngala za tirigu.
Zidzakhala ngati mmene zimakhalira munthu akamakunkha tirigu mʼchigwa cha Arefai.+
6 Mʼdzikomo mudzangotsala zokunkha zokha
Ngati mmene zimatsalira mumtengo wa maolivi akaugwedeza:
Panthambi imene ili pamwamba kwambiri pamangotsala maolivi awiri kapena atatu okha akupsa.
Panthambi zake zobala zipatso pamangotsala maolivi 4 kapena 5 okha,”+ akutero Yehova, Mulungu wa Isiraeli.
7 Tsiku limenelo, munthu adzayangʼana kumwamba, kwa amene anamupanga ndipo maso ake adzayangʼanitsitsa Woyera wa Isiraeli. 8 Iye sadzayangʼana maguwa a nsembe,+ omwe ndi ntchito ya manja ake.+ Sadzayangʼanitsitsa zinthu zimene zala zake zinapanga, kaya ndi mizati yopatulika* kapena maguwa ofukizirapo zonunkhira.
9 Tsiku limenelo mizinda yake yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri idzakhala ngati malo amene angosiyidwa mʼnkhalango.+
Idzakhala ngati nthambi imene anthu anangoisiya chifukwa cha Aisiraeli,
Ndipo idzakhala chipululu.
11 Masana umamanga mpanda bwinobwino kuzungulira munda wakowo,
Ndipo mʼmawa umachititsa kuti mbewu yako iphuke.
Koma zokolola zake zidzasowa pa tsiku la matenda ndi ululu wosachiritsika.+
12 Tamverani! Kuli chipwirikiti cha anthu ambirimbiri,
Amene akuchita mkokomo ngati nyanja.
Mitundu ya anthu ikuchita chipolowe,
Ndipo phokoso lawo lili ngati mkokomo wa madzi amphamvu.
13 Mitundu ya anthu idzachita phokoso ngati mkokomo wa madzi ambiri.
Iye adzawadzudzula ndipo iwo adzathawira kutali.
Adzathamangitsidwa ngati mankhusu* ouluzika ndi mphepo mʼmapiri
Ndiponso ngati udzu wouma wouluzika ndi mphepo yamkuntho.
14 Madzulo kudzakhala zoopsa.
Kusanache, adaniwo kudzakhala kulibe.
Izi nʼzimene zidzachitikire anthu amene akutilanda zinthu zathu
Ndipo ndi cholowa cha anthu amene akuba katundu wathu.
18 Tsoka kwa dziko lamkokomo wa tizilombo tamapiko,
Limene lili mʼchigawo cha mitsinje ya ku Itiyopiya.+
2 Dzikolo limatumiza nthumwi zake kudzera panyanja,
Zimadutsa pamadzi mʼngalawa zopangidwa ndi gumbwa.* Dzikolo limanena kuti:
“Pitani, inu amithenga achangu,
Ku mtundu wa anthu ataliatali komanso akhungu losalala,
Kwa anthu amene kulikonse amaopedwa,+
Kwa mtundu wa anthu amphamvu, amene akugonjetsa mitundu ina,
Umene nthaka yake yakokoloka ndi mitsinje.”
3 Inu nonse okhala padziko lapansi,
Zimene mukuona zidzakhala ngati chizindikiro chimene chaikidwa pamapiri,
Ndipo mudzamva phokoso lofanana ndi kulira kwa lipenga.
4 Chifukwa Yehova wandiuza kuti:
“Ndidzakhala mosatekeseka nʼkumayangʼana pamalo anga okhala,*
Ndidzachita zimenezi ngati kutentha komanso kuwala kwa dzuwa,
Ngati mame amene amagwa pa nthawi yokolola, kukamatentha.
5 Chifukwa nthawi yokolola isanafike,
Mitengo ikamaliza kuchita maluwa ndipo mphesa zikamapsa,
Mphukira zidzadulidwa ndi chida chosadzira mitengo
Ndipo tiziyangoyango take tidzadulidwa nʼkuchotsedwa.
6 Onsewo adzasiyidwa kuti adyedwe ndi mbalame zamʼmapiri zodya nyama
Komanso nyama zakutchire zapadziko lapansi.
Mbalame zodya nyamazo zidzakhala zikuwadya nyengo yonse yachilimwe,
Ndipo nyama zonse zakutchire za padziko lapansi zidzakhala zikuwadya nthawi yonse yokolola.
7 Pa nthawi imeneyo, Yehova wa magulu ankhondo akumwamba adzapatsidwa mphatso,
Kuchokera ku mtundu wa anthu ataliatali komanso akhungu losalala,
Kuchokera kwa anthu amene kulikonse amaopedwa,
Kuchokera kwa mtundu wa anthu amphamvu, amene akugonjetsa mitundu ina,
Umene nthaka yake yakokoloka ndi mitsinje.
Mphatsoyo adzaibweretsa kuphiri la Ziyoni, kumene kuli dzina la Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.”+
19 Uwu ndi uthenga wokhudza Iguputo:+
Taonani! Yehova wakwera mtambo wothamanga ndipo akubwera mu Iguputo.
Milungu yopanda pake ya ku Iguputo idzanjenjemera pamaso pake,+
Ndipo mitima ya anthu a ku Iguputo idzachita mantha kwambiri.
2 “Ndidzachititsa kuti Aiguputo ayambane ndi Aiguputo anzawo.
Ndipo azidzamenyana okhaokha
Aliyense adzamenyana ndi mʼbale wake komanso munthu woyandikana naye.
Mzinda udzamenyana ndi mzinda unzake ndipo ufumu udzamenyana ndi ufumu unzake.
Iwo adzafunsira kwa milungu yopanda pake,
Kwa anthu amatsenga, kwa olankhula ndi mizimu ndiponso kwa olosera zamʼtsogolo.+
4 Ndidzapereka Iguputo mʼmanja mwa mbuye wankhanza
Ndipo mfumu yankhanza idzawalamulira,”+ akutero Ambuye woona, Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.
6 Mitsinje idzanunkha.
Ngalande za ku Iguputo zochokera mumtsinje wa Nailo zidzaphwa ndipo zidzauma.
7 Zomera zamʼmphepete mwa mtsinje wa Nailo, kumene mtsinje wa Nailo wakathera,
Komanso malo onse amʼmphepete mwa mtsinjewo odzalidwa mbewu,+ adzauma.+
Zomera zamʼmphepete mwa mtsinjewo zidzauma ndipo zidzauluzika ndi mphepo.
8 Asodzi adzalira,
Anthu oponya mbedza mumtsinje wa Nailo adzalira,
Ndipo chiwerengero cha anthu amene amaponya maukonde awo mʼmadzi chidzachepa.
9 Anthu amene amagwiritsira ntchito fulakesi* wopalapala pa ntchito yawo+
Komanso anthu owomba nsalu* zoyera adzachititsidwa manyazi.
10 Anthu ake owomba nsalu adzavutika maganizo.
Anthu onse aganyu adzamva chisoni.
11 Akalonga a ku Zowani+ ndi opusa.
Alangizi anzeru kwambiri a Farao, amapereka malangizo osathandiza.+
Koma zoona mungamuuze Farao kuti:
“Ine ndine mbadwa ya anthu anzeru,
Ndine mbadwa ya mafumu akale”?
12 Ndiye kodi anthu ako anzeruwo ali kuti?+
Akuuze, ngati akudziwa zimene Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wakonza zokhudza Iguputo.
13 Akalonga a ku Zowani achita zopusa.
Akalonga a ku Nofi*+ apusitsidwa.
Atsogoleri a mafuko ake asocheretsa Iguputo.
14 Yehova waika mzimu wachisokonezo mʼdzikolo.+
Atsogoleri awo asocheretsa Iguputo pa chilichonse chimene akuchita,
Ngati munthu woledzera amene akuterereka mʼmasanzi ake.
15 Ndipo Iguputo sadzakhala ndi ntchito iliyonse yoti achite.
Sadzakhala ndi ntchito yoti mutu kapena mchira komanso mphukira ndi udzu* zichite.
16 Pa tsiku limenelo Aiguputo adzakhala ngati akazi ndipo adzanjenjemera ndi kuchita mantha, chifukwa Yehova wa magulu ankhondo akumwamba adzatambasula dzanja loopsa kuti awapatse chilango.+ 17 Dziko la Yuda lidzakhala chinthu chochititsa mantha kwa Iguputo. Iwo akadzangomva wina akutchula dzikolo, adzachita mantha chifukwa cha zimene Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wasakha kuti awachitire.+
18 Pa tsiku limenelo padzakhala mizinda 5 mʼdziko la Iguputo yolankhula chilankhulo cha ku Kanani+ ndiponso yolumbira kuti idzakhala yokhulupirika kwa Yehova wa magulu ankhondo akumwamba. Mzinda umodzi udzatchedwa Mzinda wa Chiwonongeko.
19 Pa tsiku limenelo, pakatikati pa dziko la Iguputo padzakhala guwa lansembe la Yehova, ndipo mʼmalire mwake mudzakhala chipilala cha Yehova. 20 Zimenezi zidzakhala chizindikiro ndi umboni kwa Yehova wa magulu ankhondo akumwamba mʼdziko la Iguputo. Iwo adzalirira Yehova chifukwa cha anthu amene akuwapondereza, ndipo iye adzawatumizira mpulumutsi wamkulu amene adzawapulumutse. 21 Yehova adzadziwika bwino kwa Aiguputo, ndipo Aiguputowo adzamudziwa Yehova pa tsiku limenelo. Iwo adzapereka nsembe ndi mphatso ndipo adzachita lonjezo kwa Yehova nʼkulikwaniritsa. 22 Yehova adzalanga Iguputo.+ Adzamulanga kenako nʼkumuchiritsa. Iwo adzabwerera kwa Yehova ndipo iye adzamva kuchonderera kwawo nʼkuwachiritsa.
23 Pa tsiku limenelo, padzakhala msewu waukulu+ wochokera ku Iguputo kupita ku Asuri. Anthu a ku Asuri adzapita ku Iguputo ndipo anthu a ku Iguputo adzapita ku Asuri. Aiguputo adzatumikira Mulungu limodzi ndi Asuri. 24 Pa tsiku limenelo, anthu a ku Isiraeli adzakhala gulu lachitatu, ataphatikizana ndi Aiguputo komanso Asuri,+ amenewa adzakhala madalitso padziko lapansi, 25 chifukwa Yehova wa magulu ankhondo akumwamba adzakhala atawadalitsa nʼkuwauza kuti: “Adalitsike Aiguputo anthu anga, Asuri ntchito ya manja anga komanso Aisiraeli omwe ndi cholowa changa.”+
20 Mʼchaka chimene Tatani* anatumizidwa ku Asidodi+ ndi Mfumu Sarigoni ya Asuri, anamenyana ndi mzindawo nʼkuulanda.+ 2 Pa nthawi imeneyo Yehova analankhula kudzera mwa Yesaya+ mwana wa Amozi kuti: “Pita ukavule chiguduli chimene chili mʼchiuno mwako komanso nsapato zimene zili kuphazi kwako.” Iye anachitadi zimenezo, nʼkumayenda ali maliseche* ndiponso wopanda nsapato.
3 Kenako Yehova anati: “Mtumiki wanga Yesaya wayenda maliseche ndiponso wopanda nsapato kwa zaka zitatu, kuti akhale chizindikiro+ ndi chenjezo kwa Iguputo+ ndi Itiyopiya.+ 4 Mofanana ndi zimenezi, mfumu ya Asuri idzagwira gulu la anthu ku Iguputo+ ndi ku Itiyopiya nʼkupita nawo ku ukapolo kudziko lina. Idzagwira anyamata ndi amuna achikulire, ali opanda zovala ndi opanda nsapato, ndiponso matako awo ali pamtunda moti Iguputo adzachititsidwa manyazi. 5 Iwo adzachita mantha komanso adzachita manyazi ndi Itiyopiya amene ankamudalira ndiponso ndi Iguputo amene ankamunyadira.* 6 Pa tsiku limenelo, anthu okhala mʼdziko limeneli lamʼmphepete mwa nyanja adzanena kuti, ‘Taonani zimene zachitikira dziko limene tinkalidalira lija, kumene tinathawirako kuti litithandize ndi kutipulumutsa kwa mfumu ya Asuri! Ndiye atipulumutse ndi ndani tsopano?’”
21 Uwu ndi uthenga wokhudza chipululu chimene chili ngati nyanja:*+
Ukubwera ngati mphepo yamkuntho imene ikuwomba kumʼmwera,
Kuchokera kuchipululu, kuchokera kudziko lochititsa mantha.+
2 Ndauzidwa masomphenya ochititsa mantha akuti:
Mtundu wachinyengo ukuchita zachinyengo,
Ndipo mtundu wowononga ukuwononga.
Pita ukachite nkhondo, iwe Elamu! Kazungulire mzindawo, iwe Mediya!+
Ndidzathetsa mavuto onse amene mzindawo unachititsa.+
3 Nʼchifukwa chake ndili pa ululu woopsa.*+
Zopweteka zandigwira,
Ngati zowawa za mkazi amene akubereka.
Ndili ndi nkhawa yaikulu moti sindikumva.
Ndasokonezeka kwambiri moti sindikuona.
4 Mtima wanga ukuthamanga. Ndikunjenjemera ndi mantha.
Chisisira cha madzulo chimene ndinkachilakalaka chikundichititsa mantha.
5 Yalani patebulo ndipo muike mipando mʼmalo mwake.
Idyani komanso kumwa.+
Nyamukani akalonga inu, dzozani* chishango.
6 Chifukwa izi ndi zimene Yehova anandiuza:
“Pita, ukaike mlonda pamalo ake ndipo ukamuuze kuti azinena zonse zimene waona.”
7 Mlondayo anaona galeta lankhondo lokokedwa ndi mahatchi awiri,
Galeta lankhondo lokokedwa ndi abulu,
Galeta lankhondo lokokedwa ndi ngamila.
Iye ankayangʼanitsitsa mwatcheru kwambiri.
8 Kenako anafuula mwamphamvu ngati kubangula kwa mkango kuti:
“Inu Yehova, ine ndimaimirira tsiku lonse pansanja ya mlonda,
Ndipo usiku uliwonse ndimakhala pamalo anga olonderapo.+
9 Taonani zimene zikubwera:
Kukubwera amuna amene akwera galeta lankhondo limene likukokedwa ndi mahatchi awiri.”+
Kenako iye analankhula kuti:
“Wagwa! Babulo wagwa!+
Zifaniziro zonse zogoba za milungu yake zaphwanyidwa ndipo zili pansi.”+
10 Inu anthu anga amene mwapunthidwa ngati mbewu,
Mbewu zapamalo* anga opunthira,+
Ndakuuzani zonse zimene ndamva kwa Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Mulungu wa Isiraeli.
11 Uwu ndi uthenga wokhudza Duma:*
Ndikumva winawake akundifunsa mofuula kuchokera ku Seiri kuti:+
“Mlonda, kodi kwatsala nthawi yaitali bwanji kuti kuche?
Mlonda, kodi kwatsala nthawi yaitali bwanji kuti kuche?”
12 Mlondayo anayankha kuti:
“Mʼmawa ukubwera, ndipo usiku ukubweranso.
Ngati mukufuna kufunsa, funsani.
Ndipo mubwerenso.”
13 Uwu ndi uthenga wokhudza chipululu:*
Inu amtengatenga a ku Dedani+ oyenda pangamila,
Usiku mudzagona mʼnkhalango yamʼchipululu.
14 Mubweretse madzi podzakumana ndi munthu waludzu,
Inu anthu okhala ku dziko la Tema,+
Ndipo mubweretse chakudya kuti mudzapatse munthu amene akuthawa.
15 Chifukwa iwo athawa malupanga, athawa lupanga limene lasololedwa,
Athawa uta umene wakungidwa ndiponso zoopsya zimene zikuchitika kunkhondo.
16 Chifukwa izi ndi zimene Yehova anandiuza: “Chaka chimodzi chisanathe, mofanana ndi zaka za munthu waganyu,* ulemerero wonse wa Kedara+ udzakhala utatha. 17 Padzatsala asilikali ochepa oponya mivi ndi uta a ku Kedara, chifukwa Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena zimenezi.”
22 Uwu ndi uthenga wokhudza Chigwa cha Masomphenya:*+
Kodi chachitika nʼchiyani kuti anthu ako onse akwere pamadenga?
2 Iwe unali mzinda wodzaza ndi chipwirikiti,
Mzinda waphokoso komanso tauni yonyada.
Anthu ako amene aphedwa, sanaphedwe ndi lupanga
Kapena kufera kunkhondo.+
3 Olamulira ako onse ankhanza athawira limodzi.+
Anagwidwa kuti akhale akaidi popanda kugwiritsa ntchito uta.
Onse amene anapezeka anagwidwa kuti akhale akaidi,+
Ngakhale kuti anathawira kutali.
Musaumirire kunditonthoza
Pamene ndikulira chifukwa cha kuwonongedwa kwa mwana wamkazi wa anthu anga.+
5 Chifukwa Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Ambuye Wamkulu Koposa,
Wabweretsa tsiku lachisokonezo, lakugonjetsedwa ndiponso lothetsa nzeru+
MʼChigwa cha Masomphenya.
Kumeneko mpanda ukugwetsedwa+
Ndipo kufuula kopempha thandizo kukumveka mʼphiri.
7 Mʼzigwa zako zabwino kwambiri
Mudzadzaza magaleta ankhondo,
Ndipo mahatchi adzaima mʼmalo awo pageti,
Pa tsiku limenelo mudzayangʼana kumalo osungirako zida zankhondo amene ali ku Nyumba ya Nkhalango,+ 9 ndipo mudzaona mingʼalu yambiri ya Mzinda wa Davide.+ Mudzatunga madzi mʼdziwe lakumunsi.+ 10 Mudzawerenga nyumba za ku Yerusalemu ndipo mudzagwetsa nyumba kuti mulimbitsire mpanda wake. 11 Mudzakumba dziwe pakati pa makoma awiri, losungiramo madzi a dziwe lakale. Koma simudzadalira Wolipanga Wamkulu ndipo simudzaganizira za amene analipanga kale kwambiri.
12 Pa tsiku limenelo, Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Ambuye Wamkulu Koposa,
Adzalamula anthu kuti alire ndi kugwetsa misozi,+
Komanso kuti amete mipala ndi kuvala ziguduli.
13 Koma mʼmalomwake mukukondwera ndi kusangalala,
Mukupha ngʼombe ndi nkhosa,
Mukudya nyama ndi kumwa vinyo.+
Inu mukuti, ‘Tiyeni tidye ndi kumwa, chifukwa mawa tifa.’”+
14 Kenako Yehova wa magulu ankhondo akumwamba anandiuza kuti: “‘Tchimo ili silidzakhululukidwa mpaka anthu inu mutafa,’+ akutero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Ambuye Wamkulu Koposa.”
15 Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Pita kwa Sebina,+ kapitawo woyangʼanira nyumba ya mfumu, ndipo ukamuuze kuti, 16 ‘Kodi kuno kuli wachibale wako aliyense, ndipo kodi mʼbale wako anaikidwa kuno kuti iweyo udzigobere manda kunoko?’ Iye wagoba manda ake pamalo okwera. Akudzigobera malo opumulirako* mʼthanthwe. 17 ‘Tamvera munthu iwe! Yehova adzakuponya pansi mwamphamvu komanso adzakugwira mwamphamvu. 18 Ndithu iye adzakukulunga mwamphamvu ndipo adzakuponyera mʼdziko lalikulu ngati akuponya mpira. Iweyo udzafera kumeneko ndipo magaleta ako ankhondo aulemerero adzakhala kumeneko. Zidzakhala zochititsa manyazi ku nyumba ya mbuye wako. 19 Ndidzakuchotsa pampando wako ndipo ndidzakuchotsa pa udindo wako.
20 Pa tsiku limenelo ndidzaitana mtumiki wanga Eliyakimu,+ mwana wa Hilikiya. 21 Iyeyo ndidzamuveka mkanjo wako ndipo lamba wako ndidzamumanga mwamphamvu mʼchiuno mwake.+ Ulamuliro wako ndidzaupereka mʼmanja mwake ndipo iye adzakhala tate wa anthu okhala mu Yerusalemu ndi amʼnyumba ya Yuda. 22 Ndidzaika kiyi wa nyumba ya Davide+ paphewa pake. Iye adzatsegula ndipo palibe amene adzatseke, adzatseka ndipo palibe amene adzatsegule. 23 Ndidzamukhomerera ngati chikhomo pamalo okhalitsa. Iye adzakhala ngati mpando wachifumu waulemerero kunyumba ya bambo ake. 24 Anthu adzapachika pa iyeyo ulemerero* wonse wa nyumba ya bambo ake, mbadwa komanso ana,* ziwiya zonse zingʼonozingʼono, ziwiya zolowa ndiponso mitsuko yonse ikuluikulu.’
25 Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti: ‘Pa tsiku limenelo chikhomo chimene chinakhomedwa pamalo okhalitsa chidzachotsedwa.+ Chidzadulidwa ndipo chidzagwa pansi. Katundu amene anapachikidwa pamenepo adzagwa pansi nʼkuwonongeka, chifukwa Yehova ndi amene wanena zimenezi.’”
23 Uwu ndi uthenga wokhudza Turo:+
Lirani mofuula inu sitima zapamadzi za ku Tarisi,+
Chifukwa chakuti doko lawonongedwa ndipo simungathenso kufikapo.
Anthu amva zimenezi ali kudziko la Kitimu.+
2 Khalani chete inu anthu okhala mʼmphepete mwa nyanja.
Amalonda a ku Sidoni,+ amene amawoloka nyanja, akulemeretsani.
3 Mbewu za ku Sihori,* zokolola zakumtsinje wa Nailo,
Zimene zinkakubweretserani ndalama, zinadutsa pamadzi ambiri,+
Nʼkubweretsa phindu la anthu a mitundu ina.+
4 Chita manyazi iwe Sidoni, iwe mzinda wotetezeka umene uli mʼmbali mwa nyanja,
Chifukwa nyanja yanena kuti:
“Sindinamvepo zowawa zapobereka, ndipo sindinaberekepo,
5 Anthu adzamva chisoni chachikulu akadzamva za Turo,+
Ngati mmene anamvera chisoni atamva za Iguputo.+
6 Wolokerani ku Tarisi.
Lirani mofuula, inu anthu okhala mʼmphepete mwa nyanja.
7 Kodi uwu ndi mzinda wanu uja, umene unali wosangalala kuyambira kalekale, kuyambira pachiyambi pake?
Mapazi ake ankautengera kumayiko akutali kuti ukakhale kumeneko.
8 Ndi ndani waganiza kuti achitire Turo zinthu zimenezi,
Mzinda umene unkaveka anthu zisoti zachifumu,
Umene amalonda ake anali akalonga,
Umenenso ochita malonda ake ankalemekezedwa padziko lonse lapansi?+
9 Yehova wa magulu ankhondo akumwamba ndi amene waganiza zochita zimenezi,
Kuti athetse kukongola kwa mzindawo komanso kunyada kwake,
Kuti achititse manyazi anthu onse amene ankalemekezedwa padziko lonse lapansi.+
10 Iwe mwana wamkazi wa Tarisi, sefukira mʼdziko lako ngati kusefukira kwa mtsinje wa Nailo.
Kulibenso doko la sitima zapanyanja.+
11 Mulungu watambasulira dzanja lake panyanja.
Wagwedeza maufumu.
Yehova walamula kuti malo otetezeka a ku Foinike awonongedwe.+
Nyamuka, wolokera ku Kitimu.+
Koma ngakhale kumeneko, sukapezako mpumulo.”
Anthu awa, osati Asuri,+
Ndi amene anapanga mzindawo kuti ukhale malo okhala nyama zamʼchipululu.
Amanga nsanja zawo zomenyerapo nkhondo.
Agumula nyumba zake zachifumu zokhala ndi mpanda wolimba,+
Ndipo iwo asandutsa mzindawo kukhala bwinja lokhalokha.
15 Pa tsiku limenelo, Turo adzaiwalidwa kwa zaka 70,+ mofanana ndi zaka za moyo wa* mfumu imodzi. Pamapeto pa zaka 70 zimenezo, Turo adzakhala ngati hule wamʼnyimbo yakuti:
16 “Iwe hule amene unaiwalidwa, tenga zeze nʼkumazungulira mumzinda.
Imba zeze wakoyo mwaluso.
Imba nyimbo zambiri,
Kuti anthu akukumbukire.”
17 Pamapeto pa zaka 70, Yehova adzakumbukira Turo. Mzindawo udzayambiranso kulandira malipiro ndipo udzachita uhule ndi maufumu onse apadziko lapansi. 18 Koma phindu lake ndi malipiro akewo zidzakhala zopatulika kwa Yehova. Zinthu zimenezi sizidzasungidwa kapena kuikidwa pambali, chifukwa malipiro akewo adzakhala a anthu okhala pamaso pa Yehova, kuti anthuwo azidya mpaka kukhuta ndiponso kuti azivala zovala zokongola.+
24 Taonani! Yehova akuchotsa anthu onse mʼdziko nʼkulisiya lopanda kanthu.+
Iye wawononga* dzikolo,+ nʼkubalalitsa anthu okhala mmenemo.+
2 Zidzachitika mofanana kwa aliyense:
Kwa anthu ndi kwa wansembe,
Kwa wantchito ndi kwa mbuye wake,
Kwa wantchito wamkazi ndi kwa mbuye wake wamkazi,
Kwa wogula ndi kwa wogulitsa,
Kwa wobwereketsa ndi kwa wobwereka,
Kwa wobwereketsa ndalama ndi kwa wobwereka ndalama.+
3 Anthu onse adzachotsedwa mʼdzikolo.
Katundu yense wamʼdzikolo adzatengedwa,+
Chifukwa Yehova ndi amene wanena mawu amenewa.
4 Dzikolo likulira*+ ndipo likuwonongeka.
Nthaka ya dziko lapansi yafota ndipo ikutha.
Anthu otchuka amʼdzikolo afota.
5 Dzikolo laipitsidwa ndi anthu okhalamo,+
Chifukwa anyalanyalaza malamulo,+
Asintha malamulo+
Ndipo aphwanya pangano limene linayenera kukhalapo mpaka kalekale.*+
Nʼchifukwa chake anthu okhala mʼdzikolo achepamo,
Ndipo anthu amene atsalamo ndi ochepa kwambiri.+
7 Vinyo watsopano akulira* ndipo mtengo wa mpesa wafota,+
Anthu onse amene amasangalala mumtima mwawo akulira.+
8 Nyimbo zachisangalalo zoimbidwa ndi maseche zasiya kumveka.
Phokoso la anthu amene akusangalala latha.
Nyimbo zachisangalalo zoimbidwa ndi zeze sizikumvekanso.+
9 Anthu akumwa vinyo popanda nyimbo,
Ndipo amene akumwa mowa akuumva kuwawa.
11 Anthu akulilira vinyo mʼmisewu.
Kusangalala konse kwatha.
Chisangalalo cha dzikolo chachoka.+
13 Izi ndi zimene zidzachitike mʼdzikolo, pakati pa anthu a mitundu ina:
Adzakhala ngati zipatso zotsala mumtengo wa maolivi utagwedezedwa,+
Ndiponso ngati mphesa zokunkha zimene zatsala anthu atamaliza kukolola.+
14 Iwo adzafuula mwamphamvu,
Adzafuula mosangalala.
Adzalengeza za ulemelero wa Yehova kuchokera kunyanja.*+
15 Nʼchifukwa chake iwo adzalemekeze Yehova mʼchigawo cha kuwala.*+
Mʼzilumba zakunyanja adzalemekeza dzina la Yehova, Mulungu wa Isiraeli.+
16 Tikumva nyimbo zikuimbidwa kuchokera kumalekezero a dziko kuti:
“Ulemelero upite kwa Wolungamayo.”+
Koma ine ndikuti: “Ndatheratu! Ndatheratu ine!
Mayo ine! Anthu akupusitsa anzawo komanso kuwachitira zachinyengo.
Iwo akupitirizabe kuchitira anzawo zachinyengo ndi kuwapusitsa.”+
17 Mantha, dzenje ndi msampha zikudikira iwe, munthu wokhala mʼdzikoli.+
18 Aliyense wothawa phokoso la chinthu chochititsa mantha adzagwera mʼdzenje,
Ndipo aliyense wotuluka mʼdzenjemo adzagwidwa mumsampha.+
Chifukwa zotsekera madzi akumwamba zidzatsegulidwa,
Ndipo maziko a dziko adzagwedezeka.
20 Dzikolo likudzandira ngati munthu woledzera.
Likugwedezekera uku ndi uku ngati chisimba* chimene chikugwedezeka ndi mphepo.
Dzikolo lalemedwa ndi zolakwa zake,+
Ndipo lidzagwa moti silidzadzukanso.
21 Tsiku limenelo Yehova adzapereka chiweruzo kwa gulu lankhondo lakumwamba
Ndi kwa mafumu apadziko lapansi.
22 Iwo adzasonkhanitsidwa pamodzi
Ngati akaidi amene akuwasonkhanitsira mʼdzenje,
Ndipo adzatsekeredwa mʼndende,
Pambuyo pa masiku ochuluka adzakumbukiridwanso.
23 Mwezi wathunthu udzachita manyazi,
Ndipo dzuwa lowala lidzachita manyazi,+
Chifukwa Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wakhala Mfumu+ mʼphiri la Ziyoni+ ndi mu Yerusalemu,
Ulemerelo wake waonekera pamaso pa achikulire a anthu ake.*+
25 Inu Yehova ndinu Mulungu wanga.
Ndikukukwezani ndi kutamanda dzina lanu
Chifukwa mwachita zinthu zodabwitsa,+
Zinthu zimene munali ndi cholinga choti muzichite kuyambira kalekale,+
Mwazichita mokhulupirika+ komanso modalirika.
2 Mwasandutsa mzinda kukhala mulu wamiyala
Tauni yokhala ndi mpanda wolimba kwambiri mwaisandutsa bwinja lokhalokha.
Mzinda wachitetezo champhamvu wa anthu achilendo mwauthetsa
Ndipo sudzamangidwanso.
4 Chifukwa inu mwakhala malo otetezeka kwa munthu wonyozeka
Malo otetezeka kwa munthu wosauka pamene akukumana ndi mavuto.+
Mwakhala malo obisalirapo mvula yamkuntho
Ndiponso mthunzi wobisalirapo kutentha kwa dzuwa.+
Mwakhala wotero pamene anthu ankhanza akuwomba anzawo ngati mvula yamkuntho imene ikuwomba khoma.
5 Mofanana ndi kutentha mʼdziko lopanda madzi,
Mumathetsa phokoso la anthu achilendo.
Mofanana ndi kutentha kumene kumatha kunja kukachita mitambo,
Nayonso nyimbo ya anthu ankhanza yaletsedwa.
6 Mʼphiri ili,+ Yehova wa magulu ankhondo akumwamba adzakonzera anthu a mitundu yonse,
Phwando la zakudya zabwino kwambiri,+
Phwando la vinyo wabwino kwambiri,*
Phwando la zakudya zabwinozabwino zokhala ndi mafuta amʼmafupa,
Ndiponso la vinyo wabwino kwambiri, wosefedwa bwino.
7 Mʼphiri limeneli iye adzachotsa* chophimba chimene chikuphimba anthu a mitundu yonse
Ndi nsalu imene yakuta mitundu yonse ya anthu.
8 Iye adzameza* imfa kwamuyaya+
Ndipo Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, adzapukuta misozi pankhope zonse za anthu.+
Adzachotsa kunyozeka kwa anthu ake padziko lonse lapansi,
Chifukwa Yehova ndi amene wanena zimenezi.
9 Pa tsiku limenelo anthu akewo adzanena kuti:
“Taonani! Uyu ndi Mulungu wathu.+
Uyu ndi Yehova.
Chiyembekezo chathu chinali mwa iye.
Tiyeni tisangalale ndi kukondwera chifukwa watipulumutsa.”+
10 Dzanja la Yehova lidzateteza* phiri limeneli,+
Ndipo Mowabu adzapondedwapondedwa mʼdziko lake lomwe+
Ngati udzu umene wapondedwapondedwa nʼkukhala mulu wa manyowa.
11 Iye adzamenya mzindawo ndi manja ake
Ngati mmene munthu amamenyera madzi ndi manja ake akamasambira.
Adzathetsa kunyada kwa mzindawo+
Poumenya mwaluso ndi manja ake.
12 Ndipo mizinda yotetezeka yokhala ndi mipanda italiitali yolimba kwambiri,
Adzaigwetsera pansi.
Adzaigumula nʼkuigwetsera pansi, pafumbi penipeni.
26 Pa tsiku limenelo, mʼdziko la Yuda+ mudzaimbidwa nyimbo+ yakuti:
“Ife tili ndi mzinda wolimba.+
Chipulumutso chake chili ngati mipanda yake ndiponso ngati malo ake okwera omenyerapo nkhondo.+
3 Anthu amene amakudalirani ndi mtima wonse* mudzawateteza.
Mudzawapatsa mtendere wosatha,+
Chifukwa amadalira inu.+
5 Chifukwa iye watsitsa anthu okhala pamalo okwezeka, mzinda wokwezeka.
Mzindawo wautsitsa,
Wautsitsira pansi,
Waugwetsera pafumbi.
6 Phazi lidzaupondaponda,
Mapazi a anthu osautsika, mapazi a anthu onyozeka adzaupondaponda.”
7 Njira ya munthu wolungama ndi yowongoka.*
Chifukwa choti ndinu wowongoka mtima,
Mudzasalaza njira ya anthu olungama.
8 Inu Yehova, pamene tikutsatira njira ya ziweruzo zanu,
Chiyembekezo chathu chili pa inu.
Tikulakalaka dzina lanu komanso zimene dzinalo limaimira.*
9 Usiku ndimakulakalakani ndi mtima wanga wonse,
Inde, ndimakufunafunani ndi mtima wonse.+
Chifukwa mukaweruza dziko lapansi,
Anthu okhala mʼdzikoli amaphunzira zokhudza chilungamo.+
Ngakhale mʼdziko lochita zowongoka, iye adzachita zinthu zoipa,+
Ndipo sadzaona ulemerero wa Yehova.+
11 Inu Yehova, dzanja lanu lakwezedwa, koma iwo sakuliona.+
Iwo adzaona kuti mumakonda kwambiri anthu anu* ndipo adzachita manyazi.
Inde, moto wanu udzapsereza adani anu.
13 Inu Yehova Mulungu wathu, ife takhala tikulamuliridwa ndi ambuye ena osati inu,+
Koma timatchula dzina lanu lokha.+
14 Iwo afa. Sadzakhalanso ndi moyo.
Iwo ndi akufa ndipo sadzaukanso.+
Chifukwa inu mwawapatsa chilango
Kuti muwawononge nʼcholinga choti asadzatchulidwenso.
Mwafutukula kwambiri malire onse a dzikolo.+
16 Inu Yehova, pa nthawi ya mavuto iwo anatembenukira kwa inu kuti muwathandize.
Mutawalanga, anakhuthulira mitima yawo kwa inu mʼpemphero lonongʼona.+
17 Mofanana ndi mkazi woyembekezera amene watsala pangʼono kubereka,
Amene akulira chifukwa cha ululu wa pobereka,
Ndi mmenenso tikumvera chifukwa cha inu Yehova.
18 Ife tinali oyembekezera ndipo tinamva zowawa za pobereka,
Koma zili ngati tinabereka mphepo.
Sitinabweretse chipulumutso mʼdzikoli,
Ndipo palibe aliyense amene wabadwa kuti akhale mʼdzikoli.
19 “Anthu anu amene anafa adzakhalanso ndi moyo.
Anthu anga amene anafa adzadzuka* nʼkuimirira.+
Dzukani ndipo mufuule mosangalala,
Inu anthu okhala mʼfumbi!+
Chifukwa mame anu ali ngati mame amʼmawa,*
Ndipo dziko lapansi lidzatulutsa anthu amene anafa kuti akhalenso ndi moyo.*
21 Chifukwa taonani! Yehova akubwera kuchokera kumene amakhala
Kuti adzaimbe mlandu anthu okhala mʼdzikoli chifukwa cha zolakwa zawo,
Ndipo dzikoli lidzaonetsa poyera magazi amene linakhetsa
Ndipo silidzabisanso anthu ake amene anaphedwa.”
27 Pa tsiku limenelo, Yehova adzagwiritsa ntchito lupanga lake lakuthwa, lalikulu ndi lolimba,+
Kulanga Leviyatani,* njoka yokwawa mothamanga!
Adzalanga Leviyatani, njoka yoyenda mokhotakhota,
Ndipo adzapha chinjoka chachikulu chokhala mʼnyanja.
2 Pa tsiku limenelo mudzaimbire mkaziyo* nyimbo yakuti:
“Iwe ndiwe munda wa mpesa wotulutsa vinyo wathovu.+
3 Ine Yehova ndikulondera mkaziyo.+
Ndimamuthirira nthawi zonse.+
Ndimamulondera masana ndi usiku,
Kuti wina aliyense asamuvulaze.+
Ngati munthu wina ataika zitsamba zaminga ndi udzu pamaso panga,
Ndidzazipondaponda nʼkuziwotcha nthawi imodzi ndipo ndidzamenyana naye.
5 Apo ayi, iye athawire kumalo anga otetezeka.
Akhazikitse mtendere ndi ine.
Iye akhazikitse mtendere ndi ine.”
6 Mʼmasiku amene akubwerawo, Yakobo adzamera mizu,
Isiraeli adzaphuka nʼkuchita maluwa,+
Ndipo iwo adzadzaza dzikolo ndi zipatso.+
7 Kodi iye akufunikira kumenyedwa ngati mmene akumenyedweramu?
Kapena kodi iye akufunikira kuphedwa ngati mmene anthu ake akuphedweramu?
8 Mudzalimbana naye ndi mfuu yoopseza pomuthamangitsa.
Iye adzamuthamangitsa ndi mphepo yake yamphamvu pa tsiku lamphepo yakumʼmawa.+
9 Choncho mwa njira imeneyi zolakwa za Yakobo zidzaphimbidwa,+
Ndipo tchimo lake likadzachotsedwa zotsatira zake zidzakhala izi:
Adzasandutsa miyala yonse yapaguwa lansembe
Kukhala ngati miyala yofewa kwambiri imene yanyenyekanyenyeka,
Ndipo sipadzatsala mizati yopatulika* kapena maguwa ofukizirapo zonunkhira.+
10 Chifukwa mumzinda wokhala ndi mpanda wolimba kwambiri mudzakhala mopanda anthu.
Malo odyetserako ziweto adzasiyidwa ndipo adzakhala opanda kanthu ngati chipululu.+
Kumeneko mwana wa ngʼombe azidzadya msipu ndiponso kugona pansi
Ndipo iye adzadya nthambi zake.+
Anthu awa samvetsa zinthu,+
Nʼchifukwa chake amene anawapanga sadzawachitira chifundo,
Ndipo amene anawaumba sadzawakomera mtima.+
12 Pa tsiku limenelo Yehova adzathyola zipatso kuchokera ku Mtsinje* mpaka kukafika kukhwawa la Iguputo+ ndipo mudzasonkhanitsidwa mmodzimmodzi, inu Aisiraeli.+ 13 Pa tsiku limenelo nyanga yaikulu ya nkhosa idzalizidwa,+ ndipo anthu amene anali atatsala pangʼono kufa mʼdziko la Asuri+ ndi amene anamwazikana mʼdziko la Iguputo,+ adzabwera kudzagwadira Yehova mʼphiri loyera ku Yerusalemu.+
28 Tsoka kwa chisoti* chokongola* cha zidakwa za ku Efuraimu+
Komanso maluwa ake okongola amene akufota!
Maluwawo avalidwa ndi mzinda umene uli paphiri, pamwamba pa chigwa chachonde, kumene zidakwa zoledzera ndi vinyozo zimakhala.
2 Taonani! Yehova ali ndi winawake wamphamvu komanso wanyonga.
Mofanana ndi mvula yamabingu komanso yamatalala, mvula yamphepo yowononga,
Mofanana ndi mvula yamabingu ya madzi amphamvu osefukira,
Iye adzagwetsera pansi chisoti chaulemererocho mwamphamvu.
4 Komanso maluwa ake okongola amene akufota,
Amene avalidwa ndi mzinda umene uli paphiri, pamwamba pa chigwa chachonde,
Adzakhala ngati nkhuyu yoyambirira kucha chilimwe chisanafike.
Munthu akaiona, amaithyola nʼkuimeza mwamsanga.
5 Pa tsiku limenelo, Yehova wa magulu ankhondo akumwamba adzakhala ngati chisoti chaulemerero ndiponso ngati nkhata yamaluwa yokongola kwa anthu ake otsala.+ 6 Adzakhalanso ngati mzimu wa chilungamo kwa munthu wopereka chiweruzo, ndiponso adzapereka mphamvu kwa anthu othamangitsa adani amene afika pageti kuti adzawaukire.+
7 Amenewanso asochera chifukwa cha vinyo.
Akuyenda modzandira chifukwa cha mowa.
Wansembe ndi mneneri asochera chifukwa cha mowa.
Vinyo wawasokoneza,
Ndipo akuyenda modzandira chifukwa cha mowa.
Sakuona bwinobwino ndipo akusochera,
Komanso akulephera kusankha zinthu mwanzeru.+
8 Pamatebulo awo padzaza masanzi.
Paliponse pali masanzi okhaokha.
9 Kodi iyeyo akufuna kuti aphunzitse ndani,
Ndipo akufuna kuti afotokozere ndani uthengawo kuti aumvetsetse?
Kodi akufuna kufotokozera ana amene asiyitsidwa kumene kuyamwa,
Amene angochotsedwa kumene kubere?
10 Chifukwa ndi “lamulo pa lamulo, lamulo pa lamulo,
Mzera ndi mzera, mzera ndi mzera,*+
Apa pangʼono, apo pangʼono.”
11 Choncho iye adzalankhula kwa anthu awa kudzera mwa anthu achibwibwi* ndiponso olankhula chilankhulo chachilendo.+ 12 Iye anauzapo anthuwo kuti: “Awa ndi malo opumira. Munthu amene watopa musiyeni apume. Awa ndi malo ampumulo,” koma iwo sanafune kumvetsera.+ 13 Choncho kwa iwowo mawu a Yehova adzakhala:
14 Choncho imvani mawu a Yehova, inu anthu odzitama,
Inu atsogoleri a anthu awa mu Yerusalemu,
15 Chifukwa anthu inu mwanena kuti:
Madzi osefukira akamadutsa,
Safika kuli ife kuno,
Chifukwa bodza talisandutsa malo athu othawirako
Ndipo tabisala mʼchinyengo.”+
16 Choncho Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti:
“Ndikuika mwala woyesedwa mu Ziyoni kuti ukhale maziko,+
Umenewu ndi mwala wapakona wamtengo wapatali+ wa maziko olimba.+
Palibe munthu woukhulupirira amene adzade nkhawa.+
Mvula yamatalala idzakokolola malo othawirapo abodza,
Ndipo madzi adzasefukira pamalo obisalako.
18 Pangano lanu limene mwachita ndi Imfa lidzatha,
Ndipo mgwirizano umene mwachita ndi Manda* sudzagwira ntchito.+
Madzi amphamvu osefukira akamadzadutsa,
Adzakukokololani.
19 Nthawi iliyonse imene akudutsa,
Azidzakukokololani.+
Chifukwa azidzadutsa mʼmawa uliwonse,
Azidzadutsanso masana komanso usiku.
Zinthu zochititsa mantha ndi zimene zidzawathandize kumvetsa zimene anamva.”*
20 Chifukwa bedi lafupika kwambiri moti munthu sangathe kugonapo mowongoka bwinobwino,
Ndipo chofunda chachepa kwambiri moti sichikukwanira bwinobwino kuti munthu afunde.
21 Yehova adzaimirira ngati mmene anachitira paphiri la Perazimu.
Adzaimirira ngati mmene anachitira mʼchigwa, pafupi ndi Gibiyoni,+
Kuti achite zochita zake, zochita zake zodabwitsa,
Komanso kuti agwire ntchito yake, ntchito yake yachilendo.+
Kuti zingwe zanu asapitirize kuzimanga kwambiri,
Chifukwa ndamva kuchokera kwa Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Ambuye Wamkulu Koposa,
23 Tcherani khutu ndipo mvetserani mawu anga.
Khalani tcheru ndi kumvetsera zimene ndikunena.
24 Kodi wolima munda ndi pulawo amangokhalira kulima tsiku lonse osadzala mbewu?
Kodi amangokhalira kuphwanya zibuma ndi kusalaza dothi?+
25 Iye akamaliza kusalaza dothilo
Kodi sawazapo chitowe chakuda ndiponso kufesa chitowe chamtundu wina?
Ndipo kodi sadzala tirigu, mapira ndi balere mʼmalo ake,
27 Chifukwa chitowe chakuda sachipuntha ndi chida chopunthira,+
Ndipo pachitowe chamtundu wina sayendetsapo mawilo a ngolo yopunthira mbewu.
Mʼmalomwake, chitowe chakuda amachipuntha ndi ndodo,
Ndipo chitowe chamtundu wina amachipuntha ndi kamtengo.
28 Kodi munthu akamapuntha tirigu, amamuphwanya mpaka kukhala ufa?
Ayi, samangokhalira kupuntha tiriguyo mosalekeza.+
Ndipo akamayendetsa mawilo a ngolo yake pa tirigu ndi mahatchi ake,
Saphwanya tiriguyo.+
29 Izinso zachokera kwa Yehova wa magulu ankhondo akumwamba,
Amene zolinga zake ndi zabwino kwambiri,
29 “Tsoka kwa Ariyeli!* Tsoka kwa Ariyeli, mzinda umene Davide anamangako msasa.+
Pitirizani kuchita zikondwerero+ zanu nthawi zonse
Muzichita zimenezi chaka ndi chaka.
2 Koma Ariyeli ndidzamubweretsera mavuto,+
Ndipo padzakhala kulira komanso chisoni,+
Kwa ine, iye adzakhala ngati malo osonkhapo moto paguwa lansembe la Mulungu.+
3 Ine ndidzamanga misasa mokuzungulira mbali zonse,
Ndidzamanga mpanda wa mitengo yosongoka mokuzungulira,
Ndipo ndidzamanga malo okwera omenyerapo nkhondo kuti ndimenyane nawe.+
4 Iweyo udzatsitsidwa,
Uzidzalankhula uli pansi penipeni,
Ndipo mawu ako azidzamveka otsika chifukwa cha fumbi.
Mawu ako adzachokera mʼnthaka+
Ngati mawu a munthu wolankhula ndi mizimu,
Ndipo adzamveka ngati kulira kwa mbalame kuchokera mʼfumbi.
5 Gulu la adani ako* lidzakhala ngati fumbi losalala,+
Gulu la olamulira ankhanza lidzakhala ngati mankhusu amene akuuluzika.+
Zimenezi zidzachitika mʼkanthawi kochepa, mosayembekezereka.+
6 Yehova wa magulu ankhondo akumwamba adzatembenukira kwa iwe kuti akupulumutse
Pogwiritsa ntchito mabingu, zivomerezi, phokoso lalikulu,
Mphepo yamkuntho ndi lawi la moto wowononga.”+
7 Kenako gulu la mitundu yonse imene ikuchita nkhondo ndi Ariyeli,+
Onse amene akumenyana naye,
Amene akumumangira nsanja zomenyerapo nkhondo kuti amenyane naye
Ndiponso amene akumubweretsera mavuto,
Adzaona ngati akulota, ngati akuona masomphenya a usiku.
8 Inde, zidzachitika ngati mmene zimakhalira munthu wanjala akamalota kuti akudya,
Koma nʼkudzuka ali ndi njala.
Kapena ngati mmene zimakhalira munthu waludzu akamalota kuti akumwa madzi,
Koma nʼkudzuka atatopa komanso ali ndi ludzu.
Zidzakhalanso choncho ndi gulu la mitundu yonse
Imene ikuchita nkhondo ndi phiri la Ziyoni.+
Iwo aledzera, koma osati ndi vinyo.
Akudzandira, koma osati chifukwa cha mowa.
10 Chifukwa Yehova wakukhuthulirani mzimu wa tulo tofa nato.+
Iye watseka maso anu, amene ndi aneneri,+
Ndipo waphimba mitu yanu, imene ndi anthu amasomphenya.+
11 Kwa inu masomphenya alionse akhala ngati mawu amʼbuku limene lamatidwa kuti lisatsegulidwe.+ Akalipereka kwa munthu wodziwa kuwerenga nʼkumuuza kuti: “Werenga bukuli mokweza,” iye adzanena kuti: “Sindingathe kuliwerenga, chifukwa ndi lomatidwa.” 12 Ndipo bukulo akalipereka kwa munthu wosadziwa kuwerenga nʼkumuuza kuti: “Werenga bukuli,” iye adzayankha kuti: “Sindidziwa kuwerenga ngakhale pangʼono.”
13 Yehova wanena kuti: “Anthu awa amandiyandikira ndi pakamwa pawo pokha
Ndipo amandilemekeza ndi milomo yawo yokha,+
Koma mitima yawo aiika kutali ndi ine,
Ndiponso amandiopa chifukwa cha malamulo a anthu amene anaphunzitsidwa.+
14 Choncho, ine ndi amene ndidzachitenso zinthu zodabwitsa ndi anthu awa,+
Ndidzachita zodabwitsa mʼnjira yodabwitsa.
Nzeru za anthu awo anzeru zidzatha,
Ndipo kumvetsetsa zinthu kwa anthu awo ozindikira kudzabisika.”+
15 Tsoka kwa anthu amene amayesa kubisira Yehova mapulani awo oipa.*+
Zochita zawo amazichitira mumdima,
Ndipo amati: “Ndi ndani akutiona?
Ndi ndani akudziwa zimene tikuchita?”+
16 Ndinu osokoneza zinthu kwambiri!*
Kodi woumba zinthu ndi dongo angafanane ndi dongolo?+
Kodi chinthu chimene chinapangidwa, chinganene za amene anachipanga kuti:
“Iye uja sanandipange”?+
Komanso kodi chinthu chochita kuumbidwa chinganene za amene anachiumba kuti:
“Iye uja samvetsa zinthu”?+
17 Pangotsala kanthawi kochepa kuti Lebanoni asanduke munda wa zipatso,+
Ndipo munda wa zipatsowo udzangokhala ngati nkhalango.+
18 Tsiku limenelo, anthu amene ali ndi vuto losamva adzamva mawu amʼbuku,
Ndipo maso a anthu amene ali ndi vuto losaona adzamasuka kumdima wandiweyani ndipo adzayamba kuona.+
19 Anthu ofatsa adzasangalala kwambiri chifukwa cha Yehova,
Ndipo osauka pakati pa anthu adzasangalala chifukwa cha Woyera wa Isiraeli.+
20 Chifukwa wolamulira wankhanza sadzakhalaponso,
Wodzitama adzawonongedwa,
Ndipo anthu onse okhala tcheru kuti achitire anzawo zoipa adzawonongedwa,+
21 Amene amanamizira anzawo mlandu,
Amene amatchera misampha munthu amene akudziteteza* pa mlandu pageti lamzinda,+
Ndiponso amene amagwiritsira ntchito mfundo zopanda umboni nʼcholinga choti asaweruze mwachilungamo mlandu wa munthu wolungama.+
22 Choncho izi ndi zimene Yehova, amene anawombola Abulahamu,+ wanena ku nyumba ya Yakobo:
23 Chifukwa akaona ana ake,
Omwe ndi ntchito ya manja anga, ali naye limodzi,+
Iwo adzayeretsa dzina langa.
Inde, adzayeretsa Woyera wa Yakobo,
Ndipo adzachita mantha ndi Mulungu wa Isiraeli.+
24 Anthu amene asochera adzamvetsa zinthu,
Ndipo amene akudandaula adzalandira malangizo.”
30 Yehova wanena kuti: “Tsoka kwa ana aamuna osamvera,+
Amene amachita zofuna zawo osati zofuna zanga,+
Amene amapanga mgwirizano* koma osati motsogoleredwa ndi mzimu wanga,
Kuti awonjezere tchimo pa tchimo.
2 Iwo amapita ku Iguputo+ asanandifunse,+
Kuti akapeze chitetezo kwa Farao*
Ndiponso kuti akabisale mumthunzi wa Iguputo.
3 Koma chitetezo cha Farao chidzakhala chochititsa manyazi kwa inu,
Ndipo kubisala mumthunzi wa Iguputo kudzachititsa kuti munyozeke.+
5 Iwo adzachititsidwa manyazi
Ndi anthu amene sangawathandize chilichonse,
Opanda phindu kapena ubwino uliwonse,
Omwe ndi ochititsa manyazi ndi onyozetsa.”+
6 Uwu ndi uthenga wokhudza zilombo zokhala kumʼmwera:
Podutsa mʼdziko la mavuto ndi la zowawa,
La mkango, mkango umene ukubangula,
La mphiri ndi la njoka zouluka zaululu wamoto,*
Iwo anyamula chuma chawo pamsana pa abulu
Ndiponso katundu wawo pamalinunda a ngamila.
Koma anthuwo sadzapindula ndi zinthu zimenezi.
7 Chifukwa thandizo lochokera ku Iguputo ndi losathandiza ngakhale pangʼono.+
Choncho iye ndamutchula kuti: “Rahabi+ amene amangokhala osachita chilichonse.”
8 “Tsopano pita ukalembe zimenezi pacholembapo, iwo akuona.
Ndipo ukazilembe mʼbuku+
Kuti mʼtsogolo
Zidzakhale umboni mpaka kalekale.+
10 Iwo auza anthu oona masomphenya kuti, ‘Lekani kuona masomphenya,’
Ndipo anthu olosera zamʼtsogolo awauza kuti, ‘Musatiuze masomphenya olondola.+
Mutiuze zinthu zotikomera. Muziona masomphenya abodza.+
11 Patukani panjira. Dzerani njira ina.
Musatiuzenso za Woyera wa Isiraeli.’”+
12 Choncho Woyera wa Isiraeli wanena kuti:
“Chifukwa chakuti mwakana mawu awa,+
Mukudalira katangale komanso chinyengo
Ndipo mukukhulupirira zinthu zimenezi,+
13 Cholakwa chanuchi chidzakhala ngati mpanda wogumuka kwa inu,
Ngati mpanda wautali umene wapendekeka ndipo watsala pangʼono kugwa.
Udzagwa mwadzidzidzi mʼkanthawi kochepa.
14 Udzaphwanyika ngati mtsuko waukulu wadothi,
Udzaphwanyikiratu wonse nʼkungokhala tizidutswatizidutswa ndipo patizidutswapo sipadzapezeka ngakhale phale
Loti nʼkupalira moto
Kapena kutungira madzi pachithaphwi.”*
15 Chifukwa Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, Woyera wa Isiraeli, wanena kuti:
“Mukabwerera kwa ine nʼkukhala odekha, mudzapulumuka.
Mudzakhala amphamvu mukakhala odekha komanso mukasonyeza kuti mukundidalira.”+
Koma inu simunafune.+
16 Mʼmalomwake munanena kuti: “Ayi, ife tidzakwera mahatchi nʼkuthawa!”
Choncho mudzathawadi.
Munanenanso kuti: “Tidzakwera mahatchi othamanga kwambiri!”+
Choncho anthu amene adzakuthamangitseni adzakhala aliwiro kwambiri.+
17 Anthu 1,000 adzanjenjemera chifukwa choopsezedwa ndi munthu mmodzi.+
Mudzathawa chifukwa choopsezedwa ndi anthu 5
Moti ochepa amene adzatsale adzakhala ngati mtengo wautali wapangalawa wozikidwa pamwamba pa phiri,
Adzakhala ngati mtengo wachizindikiro wozikidwa paphiri lalingʼono.+
18 Koma Yehova akuyembekezera moleza mtima kuti akukomereni mtima,+
Ndipo adzanyamuka kuti akuchitireni chifundo,+
Chifukwa Yehova ndi Mulungu amene amaweruza mwachilungamo.+
Osangalala ndi anthu onse amene akumuyembekezera.+
19 Anthu akadzayamba kukhala ku Ziyoni, ku Yerusalemu,+ inu simudzaliranso.+ Mulungu adzakukomerani mtima akadzamva kulira kwanu kopempha thandizo. Akadzangomva kulira kwanu, nthawi yomweyo adzakuyankhani.+ 20 Ngakhale kuti Yehova adzakupatsani mavuto kuti akhale chakudya chanu ndi kuponderezedwa kuti kukhale madzi anu akumwa,+ Mlangizi wanu wamkulu adzasiya kudzibisa ndipo maso anu adzaona Mlangizi wanu wamkulu.+ 21 Makutu anu adzamva mawu kumbuyo kwanu akuti, “Njira ndi iyi.+ Yendani mʼnjira imeneyi,” kuti musasochere nʼkulowera kudzanja lamanja kapena lamanzere.+
22 Siliva amene munakutira mafano anu ogoba komanso golide amene munakutira mafano anu achitsulo,*+ mudzamuchititsa kuti akhale wonyansa. Mudzamutaya ngati mmene mkazi amene akusamba amatayira kansalu kake, ndipo mudzanena kuti: “Nyansi zimenezi!”+ 23 Mulungu adzabweretsa mvula pambewu zanu zimene munadzala munthaka,+ ndipo chakudya chochokera munthakayo chidzakhala chochuluka komanso chopatsa thanzi.*+ Pa tsiku limenelo, ziweto zanu zidzadya msipu pamalo aakulu odyetserapo ziweto.+ 24 Ngʼombe ndi abulu amene analima mundawo, zidzadya chakudya chokoma chosakaniza ndi zitsamba zowawasira, chimene mankhusu ake anauluzidwa pogwiritsa ntchito fosholo ndi chifoloko. 25 Pa tsiku limene anthu ambiri adzaphedwe ndiponso nsanja zidzagwe, paphiri lililonse lalitali ndi paphiri lililonse lalingʼono padzakhala timitsinje ndi ngalande zamadzi.+ 26 Kuwala kwa mwezi wathunthu kudzakhala ngati kuwala kwa dzuwa. Ndipo kuwala kwa dzuwa kudzakhala kwamphamvu kwambiri kuwonjezeka maulendo 7,+ ngati kuwala kwa masiku 7. Zimenezi zidzachitika pa tsiku limene Yehova adzamange mabala* a anthu ake+ amene anavulala ndi kuchiritsa mabala aakulu amene anavulala pamene ankawalanga.+
27 Taonani! Dzina la Yehova likubwera kuchokera kutali.
Likubwera ndi mkwiyo wake woyaka moto ndiponso mitambo yolemera.
Iye akulankhula mwaukali,
Ndipo lilime lake lili ngati moto wowononga.+
28 Mzimu* wa Mulungu uli ngati mtsinje wosefukira umene wafika mʼkhosi,
Kuti agwedeze mitundu ya anthu musefa wachiwonongeko.*
Ndipo pakamwa pa mitundu ya anthuwo padzamangidwa zingwe ngati zowongolera hatchi,+ zimene zidzawachititse kuti asochere.
29 Koma mudzaimba nyimbo ngati imene imaimbidwa usiku
Mukamakonzekera* chikondwerero,+
Ndipo mudzasangalala mumtima mwanu ngati munthu
Amene akuyenda, kwinaku akuimba* chitoliro
Popita kuphiri la Yehova, Thanthwe la Isiraeli.+
30 Yehova adzapangitsa kuti mawu ake aulemerero+ amveke
Ndipo adzapangitsa kuti dzanja lake+ limene likutsika ndi mkwiyo waukulu lionekere.+
Dzanjalo lidzatsika ndi moto wowononga,+
31 Chifukwa cha mawu a Yehova, dziko la Asuri lidzagwidwa ndi mantha,+
Ndipo iye adzalimenya ndi ndodo.+
32 Ulendo uliwonse umene Yehova adzakwapule Asuri
Ndi ndodo yake yoperekera chilango,
Kudzamveka kulira kwa maseche ndi azeze+
Pamene akukweza dzanja lake kuti awalange pankhondo.+
Malo amene iye wakonzawo ndi aakulu komanso ozama
Ndipo kuli moto waukulu ndi nkhuni zambiri.
Mpweya wa Yehova, womwe uli ngati mtsinje wa sulufule,
Udzayatsa malowo.
31 Tsoka kwa anthu amene amapita ku Iguputo kukapempha thandizo,+
Amene amadalira mahatchi,+
Amene amadalira magaleta ankhondo chifukwa chakuti ndi ambiri,
Komanso mahatchi ankhondo* chifukwa chakuti ndi amphamvu kwambiri.
Koma sayangʼana kwa Woyera wa Isiraeli,
Ndipo safunafuna Yehova.
2 Koma iyenso ndi wanzeru ndipo adzabweretsa tsoka,
Komanso sadzabweza mawu ake.
Iye adzaukira nyumba ya anthu ochita zoipa
Komanso amene amathandiza anthu ochita zoipa.+
Yehova akadzatambasula dzanja lake,
Aliyense amene amapereka thandizo adzapunthwa
Ndipo aliyense amene akuthandizidwa adzagwa.
Onsewo adzawonongedwa nthawi imodzi.
4 Chifukwa izi ndi zimene Yehova wandiuza:
“Mkango umalira moopseza, mkango wamphamvu umalira poteteza nyama imene wagwira.
Abusa ambirimbiri akaitanidwa kuti adzauthamangitse,
Suchita mantha ukamva mawu awo
Kapena kutekeseka chifukwa cha phokoso lawo.
Mofanana ndi zimenezi, Yehova wa magulu ankhondo akumwamba adzatsika kuti achite nkhondo
Poteteza phiri la Ziyoni ndiponso poteteza phiri lake lalingʼono.
5 Mofanana ndi mbalame imene imauluka kuti iteteze ana ake, Yehova wa magulu ankhondo akumwamba adzateteza mzinda wa Yerusalemu.+
Iye adzauteteza nʼkuupulumutsa.
Adzaonetsetsa kuti usawonongedwe ndipo adzaulanditsa.”
6 “Aisiraeli inu, bwererani kwa Mulungu amene mwamupandukira mopanda manyazi.+ 7 Chifukwa pa tsiku limenelo, aliyense wa inu adzataya milungu yake yasiliva yomwe ndi yachabechabe komanso milungu yake yagolide yopanda phindu, imene manja anu anapanga nʼkukuchimwitsani.
Iye adzathawa chifukwa cha lupangalo
Ndipo anyamata ake adzagwiritsidwa ntchito yaukapolo.
9 Thanthwe lake lidzachoka chifukwa cha mantha,
Ndipo akalonga ake adzachita mantha chifukwa cha chizindikiro,” akutero Yehova,
Amene kuwala kwake kuli mu Ziyoni* ndiponso amene ngʼanjo yake ili mu Yerusalemu.
2 Aliyense adzakhala ngati malo obisalirapo mphepo,
Malo obisalirapo* mvula yamkuntho,
Ngati mitsinje yamadzi mʼdziko lopanda madzi,+
Ndiponso ngati mthunzi wa thanthwe lalikulu mʼdziko louma.
3 Pa nthawiyo maso a anthu amene akutha kuona sadzatsekeka,
Ndipo makutu a anthu amene amamva adzamvetsera mwatcheru.
4 Mtima wa anthu opupuluma udzaganizira mofatsa kuti udziwe zinthu,
Ndipo ngakhale lilime la anthu achibwibwi lidzalankhula bwinobwino komanso zinthu zomveka.+
5 Munthu wopusa sadzatchedwanso wopatsa,
Ndipo munthu wopanda khalidwe sadzatchedwa wolemekezeka,
6 Chifukwa munthu wopusa adzalankhula zinthu zopanda nzeru,
Ndipo mtima wake udzaganiza zochita zinthu zopweteka ena.+
Iye adzachita zimenezi kuti alimbikitse mpatuko* komanso kuti azinenera Yehova zinthu zoipa,
Kuti achititse munthu wanjala kukhala wopanda chakudya
Ndiponso munthu waludzu kukhala wopanda chilichonse choti amwe.
7 Munthu wamakhalidwe oipa, njira zake nʼzoipa.+
Iye amalimbikitsa anthu kuchita khalidwe lochititsa manyazi
Nʼcholinga choti asokoneze munthu wozunzika ndi wosauka pogwiritsa ntchito mabodza,+
Ngakhale pamene munthuyo akunena zoona.
8 Koma munthu wopatsa amakhala ndi zolinga zochita zinthu mowolowa manja,
Ndipo nthawi zonse zochita zake zimasonyeza kuti ndi wopatsa.
9 “Inu akazi ochita zinthu motayirira, nyamukani ndipo mvetserani mawu anga!
Inu ana aakazi osasamala,+ mvetserani zimene ndikunena!
10 Pakangodutsa chaka chimodzi, inu amene mumachita zinthu mosasamala mudzadzidzimuka,
Chifukwa sipadzakhala mphesa zilizonse zimene zasonkhanitsidwa ngakhale nyengo yokolola mphesa itatha.+
11 Njenjemerani, inu akazi ochita zinthu motayirira!
Dzidzimukani, inu ochita zinthu mosasamala!
Vulani nʼkukhala maliseche,
Ndipo muvale ziguduli mʼchiuno mwanu.+
12 Dzimenyeni pachifuwa pomva chisoni
Chifukwa cha kuwonongeka kwa minda yachonde ndi minda ya mpesa.
13 Panthaka ya anthu anga padzamera zitsamba zaminga.
Zidzamera panyumba zonse zimene kale zinali zodzaza ndi chisangalalo,
Inde, pamzinda umene kale unali wodzaza ndi chikondwerero.+
Ofeli+ ndi nsanja ya mlonda zasanduka chipululu mpaka kalekale.
Zasanduka malo amene abulu amʼtchire akusangalalako,
Komanso malo odyetserako ziweto,+
15 Mpaka mzimu utatsanulidwa pa ife kuchokera kumwamba,+
Ndiponso chipululu chitakhala munda wa zipatso,
Komanso munda wa zipatsowo utayamba kuoneka ngati nkhalango.+
16 Zikadzatero, mʼchipululumo mudzakhala chilungamo,
Ndipo mʼmunda wa zipatsowo mudzakhalanso chilungamo.+
17 Zotsatira za chilungamo chenicheni zidzakhala mtendere,+
Ndipo chilungamo chenicheni chidzabweretsa bata komanso chitetezo chosatha.+
18 Anthu anga adzakhala pamalo amtendere,
Adzakhala pamalo otetezeka komanso pamalo abata ndi ampumulo.+
19 Koma matalala adzawononga nkhalango yonse,
Ndipo mzinda wonse udzasalazidwa.
20 Osangalala ndinu amene mukudzala mbewu mʼmphepete mwa madzi onse,
Amene mukumasula ngʼombe yamphongo ndi bulu.”+
33 Tsoka kwa iwe amene umawononga ena koma iwe sunawonongedwe,+
Iwe amene umachitira ena zachinyengo pamene iwe sunachitiridwe zachinyengo.
Ukadzangomaliza kuwononga ena, iwenso udzawonongedwa.+
Ukadzangomaliza kuchitira ena zachinyengo, iwenso udzachitiridwa zachinyengo.
2 Inu Yehova, tikomereni mtima.+
Chiyembekezo chathu chili pa inu.
3 Mitundu ya anthu yathawa itamva phokoso lalikulu.
Inu mukanyamuka, mitundu ya anthu imamwazikana.+
4 Mofanana ndi dzombe lanjala limene limawononga chilichonse, zinthu zimene inu munalanda anthu ena zidzalandidwa
Anthu adzathamanga ngati chigulu cha dzombe kudzazitenga.
5 Yehova adzakwezedwa,
Chifukwa amakhala pamalo apamwamba.
Iye adzadzaza Ziyoni ndi chilungamo.
6 Mʼmasiku anu, iye adzachititsa kuti muzimva kuti ndinu otetezeka.
Chimene amaona kuti ndi chamtengo wapatali
Ndi chipulumutso chake chachikulu,+ nzeru, kudziwa zinthu komanso kuopa Yehova.+
7 Taonani! Anthu awo otchuka akulira mofuula mʼmisewu.
Amithenga amtendere akulira mopwetekedwa mtima.
8 Mʼmisewu ikuluikulu mulibe aliyense.
Palibe munthu aliyense amene akuyenda mʼnjira.
9 Dzikolo likulira* ndipo lafota.
Lebanoni wachita manyazi+ ndipo wawola.
Sharoni wakhala ngati chipululu
Ndipo Basana ndi Karimeli akuyoyola masamba awo.+
11 Munali ndi pakati pa udzu wouma ndipo mwabereka mapesi.
Mzimu wanu udzakupserezani ngati moto.+
12 Mitundu ya anthu idzakhala ngati zinthu zimene zimatsalira laimu akawotchedwa.
Iwo adzayaka ndi moto ngati minga zimene zasadzidwa.+
13 Inu amene muli kutali, imvani zimene ndikufuna kuchita.
Ndipo inu amene muli pafupi, vomerezani kuti ndine wamphamvu.
‘Ndi ndani wa ife amene angakhale pamene pali moto wowononga?+
Ndi ndani wa ife amene angakhale pafupi ndi moto umene sungazimitsike?’
15 Ndi amene amayenda mʼchilungamo nthawi zonse,+
Amene amalankhula zoona,+
Amene amakana kupeza phindu pochita zinthu mosaona mtima komanso mwachinyengo,
Amene manja ake amakana chiphuphu, mʼmalo mochilandira,+
Amene amatseka makutu ake kuti asamve nkhani zokhudza kukhetsa magazi,
Ndiponso amene amatseka maso ake kuti asaone zinthu zoipa.
16 Iye adzakhala pamalo okwera.
Malo ake othawirako otetezeka* adzakhala mʼmatanthwe movuta kufikamo.
Iye adzapatsidwa chakudya
Ndipo madzi ake sadzatha.”+
17 Maso ako adzaona ulemerero wa mfumu.
Adzaona dziko lakutali.
18 Mumtima mwako udzaganizira mozama za chinthu choopsa kuti:
“Kodi mlembi ali kuti?
Kodi ali kuti amene ankapereka msonkho uja?+
Kodi amene ankawerenga nsanja uja ali kuti?”
19 Anthu achipongwe simudzawaonanso,
Anthu amene chilankhulo chawo nʼchovuta kumva,*
Anthu achibwibwi amene simungamvetse zimene akulankhula.+
20 Taonani Ziyoni, mzinda umene timachitiramo zikondwerero zathu.+
Maso anu adzaona kuti Yerusalemu ndi malo okhalamo abata,
Tenti imene sidzachotsedwa.+
Zikhomo zake sizidzazulidwa
Ndipo zingwe zake sizidzadulidwa.
21 Koma kumeneko, Yehova Wolemekezeka
Adzakhala malo a mitsinje ndi a ngalande zikuluzikulu kwa ife.
Malo amene sitima zankhondo sizidzapitako
Komanso amene sitima zikuluzikulu sizidzadutsako.
22 Chifukwa Yehova ndi Woweruza wathu,+
Yehova ndi Wotipatsa Malamulo,+
Yehova ndi Mfumu yathu.+
Iye ndi amene adzatipulumutse.+
23 Zingwe zanu zidzakhala zosamanga.
Sizidzalimbitsa mtengo wautali wapasitima kapena kutambasula chinsalu chake.
Pa nthawi imeneyo adzagawana zinthu zambirimbiri zimene analanda adani awo.
Ngakhale anthu olumala adzatenga katundu wambiri amene alanda adani awo.+
24 Ndipo palibe munthu wokhala mʼdzikolo amene adzanene kuti: “Ine ndikudwala.”+
Anthu okhala mʼdzikolo adzakhululukidwa machimo awo.+
34 Bwerani pafupi kuti mumve, inu mitundu ya anthu,
Mvetserani, inu anthu a mitundu ina.
Dziko lapansi ndi zonse zimene zili mmenemo zimvetsere,
Nthaka yapadziko lapansi ndi zonse zimene zili pamenepo.
Iye adzawawononga
Ndipo adzawapha.+
4 Magulu onse ankhondo akumwamba adzawola,
Ndipo kumwamba kudzapindidwa ngati mpukutu.
Magulu awo onse ankhondo adzafota nʼkugwa,
Ngati mmene masamba ofota amathothokera pamtengo wa mpesa
Ndiponso ngati mmene nkhuyu yonyala imathothokera mumtengo wa mkuyu.
5 “Chifukwa lupanga langa lidzakhala magazi okhaokha kumwambako.+
Lupangalo lidzatsikira pa Edomu kuti lipereke chiweruzo,+
Lidzatsikira pa anthu amene ndikufuna kuwawononga.
6 Yehova ali ndi lupanga. Lupangalo lidzakhala magazi okhaokha.
Lidzakhala mafuta okhaokha,+
Lidzakhala ndi magazi a nkhosa zamphongo zingʼonozingʼono komanso a mbuzi,
Lidzakhala ndi mafuta a impso za nkhosa zamphongo.
Chifukwa Yehova adzapereka nsembe ku Bozira,
Adzapha nyama zambiri mʼdziko la Edomu.+
7 Ngʼombe zamphongo zamʼtchire zidzapita nawo limodzi,
Ngʼombe zingʼonozingʼono zamphongo zidzapita limodzi ndi zamphamvu.
Dziko lawo lidzakhala magazi okhaokha,
Ndipo fumbi lamʼdziko lawo lidzanona ndi mafuta.”
8 Chifukwa Yehova ali ndi tsiku lobwezera adani ake,+
Chaka chopereka chilango chifukwa cha zolakwa zimene Ziyoni anachitiridwa.+
9 Mitsinje yake* idzasintha nʼkukhala phula,
Fumbi lake lidzakhala sulufule,
Ndipo dziko lake lidzakhala ngati phula limene likuyaka.
10 Usiku kapena masana motowo sudzazimitsidwa.
Utsi wake udzapitiriza kukwera mʼmwamba mpaka kalekale.
Dzikolo lidzakhala lowonongedwa ku mibadwomibadwo.
Mpaka muyaya, palibe amene adzadutsemo.+
11 Mbalame ya vuwo komanso nungu zidzakhala kumeneko,
Akadzidzi a makutu ataliatali ndi akhwangwala azidzakhala kumeneko.
Mulungu adzayeza dzikolo ndi chingwe choyezera komanso miyala yoyezera
Posonyeza kuti mʼdzikoli simudzakhala aliyense komanso lidzakhala lopanda ntchito.
12 Palibe aliyense wochokera pa anthu ake olemekezeka amene adzakhale mfumu,
Ndipo akalonga ake onse adzatha.
13 Minga zidzamera pansanja zake zokhala ndi mpanda wolimba,
Zomera zoyabwa ndi zitsamba zaminga zidzamera pamalo ake otetezeka.
Iye adzakhala malo okhala mimbulu,+
Ndi malo obisalamo nthiwatiwa.
14 Nyama zamʼchipululu zidzakumana ndi nyama zolira mokuwa,
Ndipo mbuzi yamʼtchire idzaitana inzake.*
Inde, mbalame yotchedwa lumbe izidzakhala kumeneko ndipo idzapeza malo opumulirako.
15 Kumeneko, njoka yodumpha idzakonzako chisa chake nʼkuikira mazira,
Ndipo idzaswa tiana nʼkutisonkhanitsa pansi pa mthunzi wake.
Inde, mbalame zotchedwa akamtema zidzasonkhana kumeneko, iliyonse ndi mwamuna wake.
16 Fufuzani mʼbuku la Yehova ndipo muwerenge mokweza:
Palibe ndi imodzi yomwe imene idzasowe.
Palibe imene idzasowe mwamuna,
Chifukwa pakamwa pa Yehova ndi pamene palamula,
Ndipo mzimu wake ndi umene wazisonkhanitsa pamodzi.
Malowo adzakhala awo mpaka kalekale.
Zidzakhala kumeneko ku mibadwo yonse.
35 Chipululu ndi dziko louma zidzasangalala,+
Dera lachipululu lidzakondwa ndipo lidzachita maluwa ambiri.*+
Anthu adzaona ulemerero wa Yehova ndi kukongola kwa Mulungu wathu.
4 Amene ali ndi nkhawa mumtima mwawo muwauze kuti:
“Limbani mtima. Musachite mantha.
Chifukwa Mulungu wanu adzabwera nʼkudzabwezera adani anu.
Mulungu adzabwera kudzapereka chilango.+
Iye adzabwera ndipo adzakupulumutsani.”+
5 Pa nthawi imeneyo, maso a anthu amene ali ndi vuto losaona adzatsegulidwa,+
Ndipo makutu a anthu amene ali ndi vuto losamva adzayamba kumva.+
6 Pa nthawi imeneyo, munthu wolumala adzadumpha ngati mmene imachitira mbawala,+
Ndipo lilime la munthu wosalankhula lidzafuula mosangalala.+
Mʼchipululu mudzatumphuka madzi,
Ndipo mʼdera lachipululu mudzayenda mitsinje.
7 Malo ouma chifukwa cha kutentha adzakhala dambo la madzi,
Ndipo malo aludzu adzakhala ndi akasupe amadzi.+
Munthu wodetsedwa sadzayenda mumsewu umenewo.+
Amene adzayendemo ndi munthu yekhayo amene ali woyenerera.
Palibe munthu wopusa amene adzayende mumsewu umenewo.
9 Mmenemo simudzakhala mkango
Ndipo nyama zolusa zakutchire sizidzafikamo.
10 Anthu amene Yehova anawawombola adzabwerera+ ndipo adzafika ku Ziyoni akufuula mosangalala.+
Chisangalalo chosatha chidzakhala ngati chisoti chachifumu kumutu kwawo.+
Adzakhala okondwa ndi osangalala
Ndipo chisoni ndi kubuula zidzachoka.+
36 Mʼchaka cha 14 cha Mfumu Hezekiya, Senakeribu mfumu ya Asuri+ anabwera kudzaukira mizinda yonse ya Yuda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri, ndipo analanda mizindayo.+ 2 Kenako mfumu ya Asuri inatumiza Rabisake*+ kwa Mfumu Hezekiya ku Yerusalemu. Inamutumiza kuchokera ku Lakisi+ ndi gulu lalikulu la asilikali. Iwo anakaima pafupi ndi ngalande yochokera kudziwe lakumtunda,+ limene lili pamsewu waukulu wopita kumalo a wochapa zovala.+ 3 Kenako Eliyakimu+ mwana wa Hilikiya amene anali woyangʼanira banja lachifumu, Sebina+ mlembi ndi Yowa mwana wa Asafu wolemba zochitika, anapita kukakumana naye.
4 Choncho Rabisake anawauza kuti: “Mukauze Hezekiya kuti, ‘Mfumu yaikulu, mfumu ya Asuri yanena kuti: “Kodi ukudalira chiyani?+ 5 Iwe ukunena kuti, ‘Ine ndili ndi pulani komanso mphamvu zoti zindithandize pankhondo.’ Koma zimenezi nʼzabodza. Kodi ukudalira ndani kuti undipandukire?+ 6 Ukudalira thandizo la Iguputo, bango lophwanyika loti munthu ataligwira kuti alitsamire, lingamucheke mʼmanja. Ndi mmene zilili ndi Farao mfumu ya Iguputo kwa onse omudalira.+ 7 Ngati mungandiuze kuti, ‘Tikudalira Yehova Mulungu wathu,’ kodi iyeyo si amene Hezekiya wamuchotsera malo ake okwezeka ndi maguwa ake ansembe+ nʼkuuza Yuda ndi Yerusalemu kuti, ‘Muzigwada patsogolo pa guwa lansembe iliʼ?”’+ 8 Ndiye ubetcherane ndi mbuye wanga, mfumu ya Asuri+ ndipo ine ndikupatsa mahatchi 2,000 kuti tione ngati iweyo ungathe kupeza okwerapo. 9 Kodi ungathe bwanji kuthamangitsa bwanamkubwa mmodzi, yemwe ndi mtumiki wotsika kwambiri wa mbuye wanga, pamene iweyo ukuchita kudalira Iguputo kuti akupatse magaleta ndi okwera pamahatchi? 10 Kodi ukuganiza kuti ndabwera kudzawononga dziko lino popanda chilolezo cha Yehova? Yehova weniweniyo wandiuza kuti, ‘Pita ukamenyane ndi dzikolo ndipo ukaliwononge.’”
11 Atamva zimenezi, Eliyakimu, Sebina+ ndi Yowa anauza Rabisake+ kuti: “Chonde lankhulani ndi ife atumiki anu mʼchilankhulo cha Chiaramu*+ chifukwa timachimva. Musalankhule nafe mʼchilankhulo cha Ayuda, kuti anthu amene ali pamakomawa asamve.”+ 12 Koma Rabisake anawayankha kuti: “Kodi mbuye wanga wandituma kuti uthengawu ndidzauze mbuye wanu ndi inuyo basi? Kodi sananditumenso kwa amuna amene akhala pamakomawo, amene adzadye chimbudzi chawo ndi kumwa mkodzo wawo limodzi ndi inuyo?”
13 Kenako Rabisake anaimirira nʼkulankhula mokweza mʼchilankhulo cha Ayuda+ kuti: “Imvani mawu a mfumu yaikulu, mfumu ya Asuri.+ 14 Mfumuyo yanena kuti, ‘Musalole kuti Hezekiya akupusitseni, chifukwa sangathe kukupulumutsani.+ 15 Musalole kuti Hezekiya akuchititseni kudalira Yehova,+ pokuuzani kuti: “Ndithu Yehova atipulumutsa ndipo mzindawu superekedwa mʼmanja mwa mfumu ya Asuri.” 16 Musamvere Hezekiya chifukwa mfumu ya Asuri yanena kuti: “Tiyeni tigwirizane zamtendere ndipo ingonenani kuti mwagonja. Mukatero, aliyense azidya zochokera mumtengo wake wa mpesa ndi mumtengo wake wa mkuyu komanso azimwa madzi apachitsime chake, 17 mpaka ine nditabwera kudzakutengani nʼkupita nanu kudziko lofanana ndi lanulo,+ dziko la mbewu ndi la vinyo watsopano, dziko la mkate ndi minda ya mpesa. 18 Musalole kuti Hezekiya akupusitseni ponena kuti, ‘Yehova atipulumutsa.’ Kodi pali mulungu aliyense amene wakwanitsa kupulumutsa anthu ake mʼmanja mwa mfumu ya Asuri?+ 19 Kodi milungu ya Hamati ndi Aripadi+ ili kuti? Nanga milungu ya Sefaravaimu+ ili kuti? Kodi yapulumutsa Samariya mʼmanja mwanga?+ 20 Ndi mulungu uti pa milungu yonse ya mayiko amenewa, amene wapulumutsa dziko lake mʼmanja mwanga, kuti Yehova athe kupulumutsa Yerusalemu mʼmanja mwanga?”’”+
21 Koma anthuwo anangokhala chete, osamuyankha chilichonse, chifukwa mfumu inawalamula kuti, “Musakamuyankhe.”+ 22 Ndiyeno Eliyakimu mwana wa Hilikiya amene ankayangʼanira banja lachifumu,* Sebina+ mlembi ndi Yowa mwana wa Asafu wolemba zochitika, anapita kwa Hezekiya atangʼamba zovala zawo ndipo anamuuza zomwe Rabisake ananena.
37 Mfumu Hezekiya itangomva zimenezi, inangʼamba zovala zake nʼkuvala chiguduli. Itatero inapita mʼnyumba ya Yehova.+ 2 Kenako inatuma Eliyakimu amene ankayangʼanira banja lachifumu,* Sebina mlembi ndi akuluakulu a ansembe, onse atavala ziguduli, kuti apite kwa mneneri Yesaya,+ mwana wa Amozi. 3 Iwo anamuuza kuti: “Hezekiya wanena kuti, ‘Lero ndi tsiku la zowawa,* lonyozedwa ndi lochititsidwa manyazi. Chifukwa tili ngati akazi amene atsala pangʼono kubereka,* koma alibe mphamvu zoti aberekere.+ 4 Mwina Yehova Mulungu wanu amva mawu a Rabisake, amene mbuye wake mfumu ya Asuri yamutuma kuti adzanyoze Mulungu wamoyo.+ Ndipo amulanga chifukwa cha mawu amene Yehova Mulungu wanu wamva. Choncho inuyo mupemphere+ mʼmalo mwa anthu amene atsala.’”+
5 Choncho atumiki a Mfumu Hezekiya anapita kwa Yesaya.+ 6 Ndiyeno Yesaya anawauza kuti: “Mukauze mbuye wanu kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Usachite mantha+ chifukwa cha mawu amene wamva, amene atumiki a mfumu ya Asuri+ alankhula pondinyoza. 7 Ndiika maganizo* mwa iye ndipo adzamva nkhani inayake nʼkubwerera kudziko lake.+ Ndidzachititsa kuti akaphedwe ndi lupanga mʼdziko lakelo.”’”+
8 Rabisake atamva kuti mfumu ya Asuri yachoka ku Lakisi anabwerera kwa mfumuyo ndipo anaipeza ikumenyana ndi Libina.+ 9 Tsopano mfumuyo inamva zokhudza Mfumu Tirihaka ya Itiyopiya kuti: “Wabwera kudzamenyana nanu.” Itangomva zimenezo, inatumizanso uthenga kwa Hezekiya+ wakuti: 10 “Mukauze Hezekiya mfumu ya Yuda kuti, ‘Mulungu wako amene ukumudalira asakunamize, ponena kuti: “Yerusalemu saperekedwa mʼmanja mwa mfumu ya Asuri.”+ 11 Iweyo wamva zimene mafumu a Asuri anachitira mayiko onse, kuti anawawononga.+ Ndiye iweyo ukuona ngati upulumuka? 12 Kodi milungu ya mitundu imene makolo anga anaiwononga inawapulumutsa?+ Kodi inapulumutsa Gozani, Harana,+ Rezefi ndi anthu a ku Edeni amene anali ku Tela-sara? 13 Ili kuti mfumu ya Hamati, mfumu ya Aripadi ndiponso mfumu ya mzinda wa Sefaravaimu,+ wa Hena ndi wa Iva?’”
14 Hezekiya anatenga makalatawo mʼmanja mwa anthuwo nʼkuwawerenga. Kenako iye anapita nawo kunyumba ya Yehova nʼkuwatambasula pamaso pa Yehova.+ 15 Ndiyeno Hezekiya anayamba kupemphera kwa Yehova+ kuti: 16 “Inu Yehova wa magulu ankhondo akumwamba,+ Mulungu wa Isiraeli, wokhala pamwamba* pa akerubi, inu nokha ndinu Mulungu woona wa maufumu onse apadziko lapansi. Inuyo munapanga kumwamba ndi dziko lapansi. 17 Tcherani khutu lanu, inu Yehova, mumve.+ Tsegulani maso anu, inu Yehova, muone.+ Imvani mawu onse amene Senakeribu watumiza onyoza Mulungu wamoyo.+ 18 Nʼzoonadi Yehova, kuti mafumu a Asuri awononga mayiko onse,+ ndi dziko lawo lomwe. 19 Aponya milungu yawo pamoto,+ chifukwa sinali milungu, koma ntchito ya manja a anthu,+ mitengo ndi miyala. Nʼchifukwa chake anatha kuiwononga. 20 Tsopano inu Yehova Mulungu wathu, tipulumutseni mʼmanja mwake, kuti maufumu onse apadziko lapansi adziwe kuti inu nokha Yehova, ndinu Mulungu.”+
21 Ndiyeno Yesaya mwana wa Amozi anatumiza uthenga kwa Hezekiya wakuti: “Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Chifukwa chakuti wapemphera kwa ine za Senakeribu mfumu ya Asuri,+ 22 awa ndi mawu otsutsana naye amene Yehova wanena:
“Namwali, mwana wamkazi wa Ziyoni,* wakunyoza ndipo wakunyodola.
Mwana wamkazi wa Yerusalemu* wakupukusira mutu.
23 Kodi ndi ndani amene iwe wamutonza+ ndi kumunyoza?
Ndi ndani amene iwe wamulankhula mokweza,+
Ndiponso kumukwezera maso ako onyada?
Ndi Woyera wa Isiraeli!+
24 Kudzera mwa atumiki ako, wanyoza Yehova+ ndipo wanena kuti,
‘Ndi magaleta anga ankhondo ambiri,
Ndidzakwera pamwamba pa mapiri,+
Ndidzafika kumadera akutali kwambiri a Lebanoni.
Ndidzadula mitengo yake ya mkungudza italiitali, ndi mitengo yake yabwino kwambiri ya junipa.*
Ndidzalowa kumalo ake amene ali pamwamba kwambiri, kunkhalango yowirira.
26 Kodi sunamve? Ndinakonza kalekale zimene ndidzachite.
Ndinakonza zimenezi mʼmasiku amakedzana.+
Tsopano ndizichita.+
Iweyo udzasandutsa mizinda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri kukhala milu ya mabwinja.+
27 Anthu okhala mʼmizindayo adzafooka.
Adzachita mantha ndiponso adzachititsidwa manyazi.
Adzakhala ngati zomera zakutchire komanso ngati udzu wanthete wobiriwira,
Ngati udzu womera padenga umene wawauka ndi mphepo yotentha yakumʼmawa.
28 Koma ine ndimadziwa ukakhala pansi, ukamatuluka ndiponso ukamalowa.+
Ndimadziwanso ukandipsera mtima,+
29 Chifukwa kundipsera mtima kwako+ ndi kufuula kwako zafika mʼmakutu mwanga.+
Choncho ndidzakola mphuno yako ndi ngowe yanga ndipo ndidzamanga zingwe zanga+ pakamwa pako.
Kenako ndidzakukoka nʼkukubweza kudzera njira imene unadutsa pobwera.”
30 Ichi chidzakhala chizindikiro chanu:* Chaka chino mudya mbewu zimene zamera zokha. Mʼchaka chachiwiri mudzadya mbewu zophuka kuchokera ku mbewu zimenezi. Koma mʼchaka chachitatu, mudzadzala mbewu nʼkukolola ndipo mudzalima minda ya mpesa nʼkudya zipatso zake.+ 31 Anthu amʼnyumba ya Yuda amene adzapulumuke, amene adzatsale,+ adzakhala ngati mitengo imene yazika mizu pansi nʼkubereka zipatso zambiri. 32 Chifukwa anthu otsala adzachokera ku Yerusalemu ndipo opulumuka adzachokera kuphiri la Ziyoni.+ Yehova wa magulu ankhondo akumwamba adzachita zimenezi modzipereka kwambiri.+
33 Choncho Yehova wanena izi zokhudza mfumu ya Asuri:+
“Sadzalowa mumzindawu+
Kapena kuponyamo muvi
Kapena kufikamo ndi chishango
Kapenanso kumanga malo okwera omenyerapo nkhondo atauzungulira.”’+
34 ‘Adzabwerera kudzera njira imene anadutsa pobwera,
Ndipo sadzalowa mumzindawu,’ watero Yehova.
35 ‘Ndidzateteza mzindawu+ ndipo ndidzaupulumutsa chifukwa cha ineyo+
Ndiponso chifukwa cha mtumiki wanga Davide.’”+
36 Ndiyeno mngelo wa Yehova anapita kumsasa wa Asuri nʼkukapha asilikali 185,000. Anthu podzuka mʼmawa, anangoona kuti onse ndi mitembo yokhayokha.+ 37 Choncho Senakeribu mfumu ya Asuri anachoka nʼkubwerera kukakhala ku Nineve.+ 38 Pamene Senakeribu ankaweramira mulungu wake Nisiroki mʼkachisi, ana ake Adarameleki ndi Sarezere anamupha ndi lupanga+ nʼkuthawira kudziko la Ararati.+ Kenako mwana wake Esari-hadoni+ anakhala mfumu mʼmalo mwake.
38 Mʼmasiku amenewo, Hezekiya anadwala mpaka kutsala pangʼono kufa.+ Ndiyeno mneneri Yesaya+ mwana wa Amozi anapita kukamuuza kuti: “Yehova wanena kuti, ‘Uza banja lako zochita, chifukwa iweyo ufa ndithu, suchira.’”+ 2 Hezekiya atamva zimenezi, anatembenukira kukhoma nʼkuyamba kupemphera kwa Yehova kuti: 3 “Yehova ndikukupemphani kuti chonde, mukumbukire+ kuti ndinayenda pamaso panu mokhulupirika ndiponso ndi mtima wonse+ komanso ndachita zabwino pamaso panu.” Kenako Hezekiya anayamba kulira kwambiri.
4 Ndiyeno Yehova analankhula ndi Yesaya kuti: 5 “Bwerera kwa Hezekiya+ ndipo ukamuuze kuti, ‘Yehova Mulungu wa Davide kholo lako wanena kuti: “Ndamva pemphero lako+ ndipo ndaona misozi yako.+ Tsopano ndiwonjezera zaka 15 pa moyo wako,*+ 6 ndipo ndidzapulumutsa iweyo ndi mzindawu mʼmanja mwa mfumu ya Asuri komanso ndidzateteza mzinda uno.+ 7 Chizindikiro chochokera kwa Yehova chosonyeza kuti Yehova adzakwaniritsadi mawu ake,+ ndi ichi: 8 Ndichititsa kuti mthunzi wa dzuwa umene wadutsa kale pamasitepe* a Ahazi, ubwerere mʼmbuyo masitepe 10.”’”+ Choncho dzuwa linabwerera mʼmbuyo masitepe 10 pamasitepe amene linali litadutsa kale.
9 Hezekiya mfumu ya Yuda atadwala nʼkuchira, analemba zotsatirazi.
Zaka zotsala za moyo wanga zidzachotsedwa.”
11 Ndinanena kuti: “Sindidzamuona Ya,* Ya sindidzamuonanso mʼdziko la amoyo.+
Anthu sindidzawaonanso
Ndikadzakhala ndi anthu okhala kudziko limene kulibe moyo.
Ndakulunga moyo wanga ngati munthu wowomba nsalu.
Mwadula moyo wanga ngati ulusi wa nsalu.
Kuyambira mʼmawa mpaka usiku mukuchititsa kuti ndithe pangʼonopangʼono.+
13 Ndadzitonthoza mpaka mʼmawa.
Mofanana ndi mkango, iye akungokhalira kuphwanya mafupa anga onse.
Kuyambira mʼmawa mpaka usiku mukuchititsa kuti ndithe pangʼonopangʼono.+
14 Ndikungokhalira kulira ngati namzeze kapena kamwana ka mbalame.+
Ndikungokhalira kubuula ngati njiwa.+
Ndatopa ndi kudikirira thandizo kuchokera kumwamba.+ Choncho ndinati:
‘Inu Yehova ine ndapanikizika kwambiri.
Chonde ndithandizeni.’+
15 Kodi ndinene kuti chiyani?
Iye walankhula ndi ine ndipo wachitapo kanthu.
Ndidzayenda modzichepetsa zaka zonse za moyo wanga
Chifukwa cha kupweteka kwa mtima wanga.*
16 ‘Inu Yehova, munthu aliyense amakhala ndi moyo chifukwa cha zinthu zimenezi,*
Ndipo mʼzinthu zimenezi, mzimu wanga umapezamo moyo.
Inu mudzabwezeretsa thanzi langa nʼkundithandiza kuti ndikhalebe ndi moyo.+
17 Mʼmalo mopeza mtendere ndinali ndi chisoni chachikulu.
Koma chifukwa chakuti mumandikonda kwambiri,
Munanditeteza kuti ndisapite kudzenje lachiwonongeko.+
Machimo anga onse mwawaponyera kumbuyo kwanu.*+
Anthu amene akutsikira kudzenje sangayembekezere kuti muwasonyeze kukhulupirika kwanu.+
19 Munthu wamoyo, amene akupuma, ndi amene angakutamandeni,
Ngati mmene ineyo ndikuchitira lero.
Bambo akhoza kuphunzitsa ana ake za kukhulupirika kwanu.+
20 Inu Yehova, ndipulumutseni,
Ndipo ine ndi anthu ena tidzaimba nyimbo zanga ndi zoimbira za zingwe+
Kunyumba ya Yehova masiku onse a moyo wathu.’”+
21 Kenako Yesaya anati: “Bweretsani keke ya nkhuyu zouma zoumba pamodzi ndipo muziike pachotupa chimene ali nacho kuti achire.”+ 22 Hezekiya anali atafunsa kuti: “Kodi chizindikiro chakuti ndidzapitadi kunyumba ya Yehova nʼchiyani?”+
39 Pa nthawi imeneyo, Merodaki-baladani mwana wa Baladani mfumu ya Babulo, anatumiza makalata ndi mphatso kwa Hezekiya+ chifukwa anamva kuti amadwala ndipo wachira.+ 2 Hezekiya analandira anthuwo mwansangala* ndipo anawaonetsa nyumba yake yosungiramo chuma.+ Anawaonetsa siliva, golide, mafuta a basamu, mafuta ena amtengo wapatali, nyumba yake yosungiramo zida zonse zankhondo ndiponso chuma chake chonse. Palibe chimene Hezekiya sanawaonetse mʼnyumba* yake ndi mu ufumu wake wonse.
3 Kenako mneneri Yesaya anapita kwa Mfumu Hezekiya nʼkuifunsa kuti: “Kodi anthu aja anena kuti chiyani, nanga anachokera kuti?” Hezekiya anayankha kuti: “Anachokera kudziko lakutali, ku Babulo.”+ 4 Atatero Yesaya anafunsa kuti: “Aona chiyani mʼnyumba mwanu?” Hezekiya anayankha kuti: “Aona chilichonse chimene chili mʼnyumba mwanga. Palibe chimene sindinawaonetse pa chuma changa.”
5 Ndiyeno Yesaya anauza Hezekiya kuti: “Imva zimene Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena, 6 ‘Tamvera, masiku akubwera pamene zinthu zonse zimene zili mʼnyumba mwako ndiponso zonse zimene makolo ako akhala akusunga mpaka lero, anthu adzazitenga nʼkupita nazo ku Babulo. Palibe chidzatsale,’+ watero Yehova.+ 7 ‘Ena mwa ana ako, amene iweyo udzabereke, adzatengedwa ndipo adzakhala nduna zapanyumba ya mfumu ya ku Babulo.’”+
8 Hezekiya atamva zimenezi anauza Yesaya kuti: “Mawu a Yehova amene mwanenawa ndi abwino.” Anapitiriza kuti: “Chifukwa mʼmasiku anga mukhala bata* ndi mtendere.”+
40 “Limbikitsani anthu anga. Ndithu alimbikitseni,” akutero Mulungu wanu.+
2 “Mulankhuleni Yerusalemu momufika pamtima.*
Muuzeni kuti ntchito imene ankagwira mokakamizidwa yatha,
Komanso kuti malipiro a zolakwa zake aperekedwa.+
Kuchokera mʼdzanja la Yehova, iye walandira malipiro okwanira* a machimo ake onse.”+
3 Winawake akufuula mʼchipululu kuti:
“Konzani njira ya Yehova!+
Mulungu wathu mukonzereni msewu wowongoka+ wodutsa mʼchipululu.+
4 Chigwa chilichonse chikwezedwe mʼmwamba,
Ndipo phiri lililonse ndi chitunda chilichonse zitsitsidwe.
Malo okumbikakumbika asalazidwe,
Ndipo malo azitunda akhale chigwa.+
5 Ulemerero wa Yehova udzaonekera,+
Ndipo anthu onse adzauonera limodzi,+
Chifukwa pakamwa pa Yehova panena.”
6 Tamvera! Winawake akunena kuti: “Lengeza mofuula!”
Wina akufunsa kuti: “Ndilengeze mofuula za chiyani?”
“Anthu onse ali ngati udzu wobiriwira.
Chikondi chawo chonse chokhulupirika chili ngati duwa lakutchire.+
Ndithu anthu ali ngati udzu wobiriwira.
Fuula mwamphamvu,
Iwe mkazi amene ukubweretsa uthenga wabwino wonena za Yerusalemu.
Fuula, usachite mantha.
Lengeza kumizinda ya ku Yuda kuti: “Mulungu wanu ali nanu.”+
10 Taonani! Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, adzabwera nʼkuonetsa mphamvu zake,
Mphoto yake ili ndi iyeyo,
Ndipo malipiro amene amapereka ali pamaso pake.+
11 Iye adzasamalira* gulu la nkhosa zake ngati mʼbusa.+
Ndi dzanja lake, adzasonkhanitsa pamodzi ana a nkhosa,
Ndipo adzawanyamulira pachifuwa pake.
Nkhosa zimene zikuyamwitsa adzazitsogolera mwachikondi.+
12 Ndi ndani anayezapo madzi onse amʼnyanja pachikhatho cha dzanja lake?+
Ndi ndani anayezapo kumwamba ndi dzanja lake?
Ndi ndani anasonkhanitsapo fumbi lonse lapadziko lapansi mʼmbale yoyezera+
Kapena kuyeza mapiri pachoyezera
Komanso zitunda pasikelo?
13 Ndi ndani amene anayezapo* mzimu wa Yehova,
Ndipo ndi ndani amene angamulangize ngati mlangizi wake?+
14 Kodi anafunsirapo nzeru kwa ndani kuti amuthandize kumvetsa zinthu?
Ndi ndani amene amamuphunzitsa njira yachilungamo,
Kapena kumuphunzitsa kuti adziwe zinthu,
Kapenanso kumusonyeza njira yokhalira womvetsadi zinthu?+
15 Taonani! Mitundu ya anthu ili ngati dontho la madzi lochokera mumtsuko,
Ndipo iye amawaona ngati fumbi limene lili pasikelo.+
Iyetu amanyamula zilumba ngati akunyamula fumbi.
16 Ngakhale mitengo yonse ya ku Lebanoni singakwane kusonkhezera moto kuti usazime,*
Ndipo nyama zake zamʼtchire nʼzosakwanira kukhala nsembe yopsereza.
17 Kwa iye, mitundu yonse ya anthu ili ngati chinthu chomwe sichinakhaleko.+
Samaiona ngati kanthu, amangoiona ngati chinthu chimene kulibeko.+
18 Kodi Mulungu mungamuyerekezere ndi ndani?+
Kodi munganene kuti amafanana ndi chiyani?+
19 Mmisiri amapanga fano lachitsulo,*
Mmisiri wina wa zitsulo amachikuta ndi golide,+
Ndipo amachipangira matcheni asiliva.
Amafunafuna mmisiri waluso
Kuti amupangire chifaniziro chosema chimene sichingagwe.+
21 Kodi simukudziwa?
Kodi simunamve?
Kodi simunauzidwe kuchokera pachiyambi?
Kodi simunamvetse umboni umene wakhalapo kuchokera pamene maziko a dziko lapansi anakhazikitsidwa?+
22 Pali winawake amene amakhala pamwamba pa dziko lapansi lomwe ndi lozungulira,+
Ndipo amene amakhala mʼdzikolo ali ngati ziwala.
Iye anatambasula kumwamba ngati nsalu yopyapyala,
Ndipo anakufutukula ngati tenti yoti azikhalamo.+
23 Iye amachotsa paudindo anthu olamulira
Ndipo amachititsa oweruza* apadziko lapansi kuoneka ngati sanakhalepo nʼkomwe.
24 Iwo ali ngati mbewu zimene zangodzalidwa kumene,
Ali ngati mbewu zimene zangofesedwa kumene,
Thunthu lawo langoyamba kumene kuzika mizu munthaka.
Mphepo yawawomba nʼkuuma
Ndipo auluzika ndi mphepo ngati mapesi.+
25 “Kodi mungandiyerekezere ndi ndani amene ndingafanane naye?” akutero Woyerayo.
26 “Kwezani maso anu kumwamba ndipo muone.
Kodi ndi ndani amene analenga zinthu zimenezi?+
Ndi amene akutsogolera gulu lonse la nyenyezi ndipo zonse amaziwerenga.
Iliyonse amaiitana poitchula dzina lake.+
Chifukwa cha kuchuluka kwa mphamvu zake zoopsa ndiponso chifukwa chakuti ali ndi mphamvu zambiri zochitira zinthu,+
Palibe iliyonse imene imasowa.
27 Nʼchifukwa chiyani iwe Yakobo, komanso nʼchifukwa chiyani iwe Isiraeli ukunena kuti,
‘Yehova sakuona zimene zikuchitika pa moyo wanga,
Ndipo Mulungu akunyalanyaza zinthu zopanda chilungamo zimene zikundichitikiraʼ?+
28 Kodi iwe sukudziwa? Kodi sunamve?
Yehova, Mlengi wa malekezero a dziko lapansi ndi Mulungu mpaka kalekale.+
Iye satopa kapena kufooka.+
Palibe amene angamvetse* nzeru zake.+
29 Iye amapereka mphamvu kwa munthu wotopa
Ndipo munthu amene alibe mphamvu amamupatsa mphamvu zambiri.+
30 Anyamata adzatopa nʼkufooka,
Ndipo amuna achinyamata adzapunthwa nʼkugwa,
31 Koma anthu amene amayembekezera Yehova adzapezanso mphamvu.
Iwo adzaulukira mʼmwamba ngati kuti ali ndi mapiko a chiwombankhanga.+
Adzathamanga koma osafooka.
Adzayenda koma osatopa.”+
Bwerani pafupi ndi ine, kenako mulankhule.+
Tiyeni tikumane ndipo ndikuweruzani.
2 Kodi ndi ndani amene wapatsa mphamvu winawake kuchokera kotulukira dzuwa,*+
Amene wamuitana mwachilungamo kuti ayandikire kumapazi ake,*
Kuti amupatse mitundu ya anthu
Ndiponso kuti amuchititse kuti agonjetse mafumu?+
Kodi ndi ndani amene amawasandutsa fumbi pogwiritsa ntchito lupanga lake,
Ndipo ndi ndani amene amawabalalitsa ngati mapesi ouluzika ndi mphepo pogwiritsa ntchito uta wake?
3 Iye amawathamangitsa, amadutsa popanda chilichonse chomusokoneza
Mʼnjira zimene mapazi ake sanayambe adutsamo.
4 Ndi ndani wachita zimenezi,
Ndi ndani waitana mibadwo kuchokera pachiyambi?
5 Zilumba zaona zimenezi ndipo zachita mantha.
Malekezero a dziko lapansi anayamba kunjenjemera.
Mitundu ya anthu inayandikira nʼkubwera.
6 Aliyense akuthandiza mnzake
Ndipo akuuza mʼbale wake kuti: “Limba mtima.”
7 Choncho mmisiri wa mitengo akulimbikitsa mmisiri wa zitsulo.+
Amene amawongola zitsulo ndi hamala
Akulimbikitsa munthu amene akusula zitsulo ndi hamala.
Ponena za ntchito yowotcherera zitsulo ndi mtovu, iye akuti: “Zili bwino.”
Kenako amakhomerera fanolo ndi misomali kuti lisagwe.
8 “Koma iwe Isiraeli, ndiwe mtumiki wanga,+
Iwe Yakobo, amene ndakusankha,+
Mbadwa* ya mnzanga Abulahamu.+
9 Iwe amene ndinakutenga kuchokera kumalekezero a dziko lapansi,+
Ndiponso iwe amene ndinakuitana kuchokera kumadera akutali a dziko lapansi.
10 Usachite mantha, chifukwa ndili ndi iwe.+
Usade nkhawa chifukwa ine ndine Mulungu wako.+
Ndikulimbitsa, ndithu ndikuthandiza,+
Ndikugwira mwamphamvu ndi dzanja langa lamanja lachilungamo.’
11 Taona! Onse amene amakupsera mtima adzachita manyazi ndipo adzanyozeka.+
Anthu amene akumenyana nawe adzawonongedwa ndipo adzatha.+
12 Anthu amene akulimbana nawe udzawafunafuna koma sudzawapeza.
Anthu amene akumenyana nawe adzakhala ngati chinthu chimene kulibeko ndipo sadzakhalanso ngati kanthu.+
13 Chifukwa ine, Yehova Mulungu wako, ndagwira dzanja lako lamanja,
Ine amene ndikukuuza kuti, ‘Usachite mantha. Ineyo ndikuthandiza.’+
14 “Usachite mantha, nyongolotsi* iwe Yakobo,+
Inu amuna a mu Isiraeli, ineyo ndikuthandizani,” akutero Yehova, Wokuwombolani,+ Woyera wa Isiraeli.
15 “Taona! Ndakusandutsa chopunthira mbewu,+
Chida chatsopano chopunthira mbewu chokhala ndi mano akuthwa konsekonse.
Udzapondaponda mapiri nʼkuwaphwanya
Ndipo zitunda udzazisandutsa mankhusu.
17 “Anthu ovutika ndi osauka akufunafuna madzi, koma sakuwapeza.
Lilime lawo lauma chifukwa cha ludzu.+
Ineyo Yehova ndidzawayankha.+
Ineyo Mulungu wa Isiraeli, sindidzawasiya.+
18 Ndidzachititsa kuti mitsinje yamadzi iyende mʼmapiri opanda zomera zilizonse+
Komanso kuti akasupe atuluke mʼzigwa.+
Chipululu ndidzachisandutsa dambo lamadzi
Ndipo dziko lopanda madzi ndidzalisandutsa akasupe amadzi.+
19 Mʼchipululu ndidzadzalamo mtengo wa mkungudza,
Mtengo wa mthethe, mtengo wa mchisu ndi mtengo wa paini.+
Mʼchigwa chamʼchipululu ndidzadzalamo mtengo wa junipa,*
Limodzi ndi mtengo wa ashi* komanso mtengo wofanana ndi mkungudza,+
20 Ndidzachita zimenezi kuti anthu onse aone ndipo adziwe,
Amve ndiponso azindikire
Kuti dzanja la Yehova ndi limene lachita zimenezi,
Ndiponso kuti Woyera wa Isiraeli ndi amene wachititsa zimenezi.”+
21 “Bweretsani kuno mlandu wanu,” akutero Yehova.
“Fotokozani mfundo zanu,” ikutero Mfumu ya Yakobo.
22 “Tipatseni umboni ndipo mutiuze zinthu zimene zidzachitike.
Tiuzeni zokhudza zinthu zakale,*
Kuti tiziganizire mozama nʼkudziwa tsogolo lake.
Kapena mutiuze zinthu zimene zikubwera.+
Inde, chitani chinachake, chabwino kapena choipa,
Kuti tidabwe tikachiona.+
Aliyense amene amasankha kukulambirani ndi wonyansa.+
25 Ine ndapatsa mphamvu winawake kuchokera kumpoto, ndipo abwera.+
Iye adzachokera kotulukira dzuwa*+ ndipo adzaitana pa dzina langa.
26 Kodi ndi ndani ananenapo zokhudza zimenezi kuchokera pachiyambi kuti tidziwe,
Kapena kuchokera kalekale kuti tinene kuti, ‘Akunena zoonaʼ?+
Ndithu palibe amene analengeza zimenezi.
Palibe amene ananena chilichonse.
Palibe amene anamva chilichonse kuchokera kwa inu.”+
27 Ine ndinali woyamba kuuza Ziyoni kuti: “Tamverani zimene zidzachitike!”+
Ndipo ku Yerusalemu ndidzatumizako munthu wobweretsa uthenga wabwino.+
28 Koma ndinapitiriza kuyangʼana, ndipo panalibe aliyense.
Pakati pa mafanowo panalibe aliyense amene akanapereka malangizo.
Ndipo ndinapitiriza kuwafunsa, koma palibe anayankha.
29 Onsewo ndi opanda ntchito.*
Ntchito zawo ndi zopanda pake.
Mafano awo opangidwa ndi zitsulo* ali ngati mphepo ndipo ndi opanda ntchito.+
42 Taonani mtumiki wanga+ amene ndikumuthandiza,
Wosankhidwa wanga+ amene amandisangalatsa,+
Iye adzabweretsa chilungamo mokhulupirika.+
4 Iye sadzafooka kapena kutaya mtima mpaka atakhazikitsa chilungamo padziko lapansi.+
Ndipo zilumba zikudikirirabe malamulo ake.*
5 Mulungu woona Yehova,
Amene analenga kumwamba ndiponso Mulungu Wamkulu amene anakutambasula,+
Amene anapanga dziko lapansi ndi zonse zimene zili mmenemo,+
Amene amapereka mpweya kwa anthu amene ali mmenemo,+
Komanso mzimu* kwa anthu amene amayenda padzikolo,+ wanena kuti:
6 “Ineyo Yehova pofuna kusonyeza chilungamo, ndinakuitana.
Ndakugwira dzanja.
Ndidzakuteteza ndipo udzakhala ngati pangano pakati pa ine ndi anthu+
Ndiponso ngati kuwala ku mitundu ya anthu,+
7 Kuti ukatsegule maso a anthu amene ali ndi vuto losaona,+
Kuti ukatulutse mkaidi mʼdzenje lamdima
Ndiponso kuti anthu amene ali mumdima akawatulutse mʼndende.+
8 Ine ndine Yehova. Dzina langa ndi limeneli.
Sindipereka ulemerero wanga kwa wina aliyense
Ndipo sindifuna kuti aliyense azitamanda zifaniziro zogoba mʼmalo mwa ine.+
9 Taonani, zinthu zimene ndinaneneratu kalekale zachitika,
Tsopano ndikulengeza zinthu zatsopano.
Zisanayambe kuonekera, ndimakuuzani.”+
10 Imbirani Yehova nyimbo yatsopano.+
Mʼtamandeni kuchokera kumalekezero a dziko lapansi,+
Inu nonse amene mumadalira nyanja komanso zonse zimene zimakhala mmenemo,
Inu zilumba ndi anthu amene amakhala mʼzilumbazo.+
Anthu amene amakhala mʼdera lamatanthwe afuule mosangalala.
Anthuwo afuule kuchokera pamwamba pa mapiri.
13 Yehova adzapita kunkhondo ngati munthu wamphamvu.+
Iye adzachita zinthu modzipereka kwambiri ngati msilikali.+
Adzafuula, inde adzafuula ngati anthu amene akupita kunkhondo.
Iye adzasonyeza kuti ndi wamphamvu kwambiri kuposa adani ake.+
14 Mulungu wanena kuti: “Ndakhala chete kwa nthawi yaitali.
Ndinangokhala phee osachita chilichonse.
Mofanana ndi mkazi amene akubereka,
Ndibuula, ndipuma movutikira komanso mwawefuwefu. Zonsezi zichitika nthawi imodzi.
15 Ndidzawononga mapiri ndi zitunda
Ndi kuumitsa zomera zonse zimene zili mmenemo.
16 Anthu amene ali ndi vuto losaona ndidzawatsogolera kuti ayende mʼnjira imene sakuidziwa.+
Ndidzawadutsitsa mʼnjira zachilendo.+
Zimenezi ndi zimene ndidzawachitire ndipo sindidzawasiya.”
17 Anthu amene akudalira zifaniziro zosema,
Amene akuuza zifaniziro zachitsulo* kuti: “Ndinu milungu yathu,”+
Adzathawa ndipo adzachita manyazi kwambiri.
18 Inu amene muli ndi vuto losamva, mvetserani.
Inu amene muli ndi vuto losaona, yangʼanani kuti muone.+
19 Kodi pali winanso amene ali ndi vuto losaona ngati mtumiki wanga,
Amene ali ndi vuto losamva ngati munthu amene ndamutuma kukapereka uthenga?
Kodi ndi ndani amene ali ndi vuto losaona ngati munthu amene wapatsidwa mphoto,
Amene saona ngakhale pangʼono ngati mtumiki wa Yehova?+
20 Umaona zinthu zambiri, koma sukhala tcheru.
Umatsegula makutu ako koma sumvetsera.+
21 Chifukwa cha chilungamo chake,
Yehova akufunitsitsa kusonyeza kuti malamulo* ake ndi apamwamba komanso aulemerero.
22 Koma awa ndi anthu amene katundu wawo wabedwa komanso kulandidwa.+
Onse agwera mʼmaenje amene sangathe kutulukamo ndipo atsekeredwa mʼndende.+
Iwo atengedwa popanda wowapulumutsa,+
Agwidwa popanda wonena kuti: “Bwererani nawo!”
23 Ndi ndani pakati panu amene adzamvetsere zinthu zimenezi?
Ndi ndani amene adzatchere khutu ndi kumvetsera zinthu zimene zidzamuthandize mʼtsogolo?
24 Ndi ndani wachititsa kuti Yakobo alandidwe katundu wake
Ndiponso kupereka Isiraeli kwa anthu olanda?
Kodi si Yehova amene iwo amuchimwira?
25 Choncho Mulungu anapitiriza kuwakhuthulira ukali ndi mkwiyo wake,
Anawabweretsera nkhondo yoopsa.+
Moto unapsereza chilichonse chimene anali nacho, koma iwo sanalabadire.+
Motowo unapitiriza kuwawotcha koma iwo sizinawakhudze.+
43 Tsopano izi ndi zimene Yehova wanena,
Mlengi wako iwe Yakobo, amene anakupanga iwe Isiraeli.+ Iye wanena kuti:
“Usachite mantha, chifukwa ine ndakuwombola.+
Ndakuitana pokutchula dzina lako.
Iwe ndiwe wanga.
Ukamadzayenda pamoto sudzapsa
Ndipo ngakhale lawi la moto silidzakuwaula.
3 Chifukwa ine ndine Yehova Mulungu wako,
Woyera wa Isiraeli, Mpulumutsi wako.
Ndapereka Iguputo kuti akhale dipo* lako.
Ndaperekanso Itiyopiya ndi Seba mʼmalo mwa iwe.
Choncho ndidzapereka anthu mʼmalo mwa iwe
Komanso mitundu ya anthu posinthanitsa ndi moyo wako.
5 Usachite mantha chifukwa ine ndili ndi iwe.+
Ndidzabweretsa mbadwa* zako kuchokera kumʼmawa,
Ndipo ndidzakusonkhanitsani pamodzi kuchokera kumadzulo.+
6 Ndidzauza kumpoto kuti, ‘Abwezere kwawo!’+
Ndipo ndidzauza kumʼmwera kuti, ‘Usawakanize.
Bweretsa ana anga aamuna kuchokera kutali komanso ana anga aakazi kuchokera kumalekezero a dziko lapansi.+
7 Bweretsa aliyense amene amatchedwa ndi dzina langa,+
Ndiponso amene ndinamulenga kuti ndipatsidwe ulemerero,
Amene ndinamuumba komanso kumupanga.’+
8 Bweretsa anthu amene saona ngakhale kuti ali ndi maso,
Ndiponso anthu osamva ngakhale kuti ali ndi makutu.+
Ndi ndani pakati pa milungu yawo amene ananena kuti zinthu zimenezi zidzachitika?
Kapena kodi angatiuze zinthu zimene zidzayambirire kuchitika?+
Abweretse mboni zawo kuti tidziwe ngati akunena zoona,
Kapena mbonizo zimvetsere nʼkunena kuti, ‘Zimenezo ndi zoona!’”+
10 “Inu ndinu mboni zanga,”+ akutero Yehova,
“Inde, mtumiki wanga amene ndamusankha,+
Kuti mundidziwe ndi kundikhulupirira,*
Komanso kuti mumvetse kuti ine sindimasintha.+
Ine ndisanakhaleko kunalibe Mulungu amene anapangidwa,
Ndipo pambuyo panga palibenso wina.+
11 Ine ndine Yehova.+ Palibenso mpulumutsi wina kupatulapo ine.”+
12 “Ine ndi amene ndinanena zimene zidzachitike, amene ndinakupulumutsani komanso amene ndinachititsa kuti zimenezi zidziwike,
Pa nthawi imene pakati panu panalibe mulungu wachilendo.+
Choncho inuyo ndinu mboni zanga, ndipo ine ndine Mulungu,” akutero Yehova.+
13 “Komanso, nthawi zonse ine sindisintha.+
Ndipo palibe amene angathe kulanda chinthu chilichonse mʼdzanja langa.+
Ndikachita chinthu, ndi ndani amene angaletse?”+
14 Yehova, Wokuwombolani,+ Woyera wa Isiraeli,+ wanena kuti:
“Chifukwa cha inu, ndidzatumiza asilikali ku Babulo ndipo adzagwetsa zotsekera mʼmageti,+
Komanso Akasidi adzalira chifukwa chopanikizika, ali mʼsitima zawo zapamadzi.+
15 Ine ndine Yehova, Woyera wanu,+ Mlengi wa Isiraeli+ ndiponso Mfumu yanu.”+
16 Izi nʼzimene Yehova wanena,
Yemwe amapanga msewu panyanja
Komanso njira ngakhale pamadzi osefukira,+
17 Amene amatsogolera magaleta ankhondo ndi mahatchi,+
Gulu lankhondo pamodzi ndi asilikali amphamvu, wanena kuti:
“Iwo adzagona pansi ndipo sadzadzukanso.+
Adzazimitsidwa ngati chingwe cha nyale.”
18 “Musakumbukire zinthu zakale,
Ndipo musamangoganizira zinthu zakumbuyo.
Kodi simukuchizindikira?
20 Zilombo zakutchire zidzandilemekeza,
Komanso mimbulu ndi nthiwatiwa,
Chifukwa ndimapereka madzi,
Ndiponso mitsinje mʼchipululu,+
Kuti anthu anga, wosankhidwa wanga,+ amwe,
21 Ndiponso kuti anthu amene ndinawapanga kuti akhale anga,
Alengeze za ulemerero wanga.+
23 Iwe sunandibweretsere nkhosa kuti zikhale nsembe zako zopsereza zathunthu
Kapena kundilemekeza ndi nsembe zako.
Ine sindinakukakamize kuti undibweretsere mphatso,
24 Iwe sunandigulire bango lonunkhira* ndi ndalama zako,
Ndipo sunandikhutitse ndi mafuta a nsembe zako.+
Mʼmalomwake, wanditopetsa ndi machimo ako
Ndipo wandilemetsa ndi zolakwa zako.+
25 Ineyo ndi amene ndikufafaniza zolakwa zako*+ chifukwa cha dzina langa,+
Ndipo machimo ako sindidzawakumbukira.+
26 Ndikumbutse, tiye tiimbane mlandu.
Fotokoza mbali yako kuti usonyeze kuti ndiwe wosalakwa.
28 Choncho ndidzadetsa akalonga apamalo oyera,
Ndidzachititsa kuti Yakobo awonongedwe
Ndipo ndidzachititsa kuti Isiraeli amunenere mawu onyoza.”+
Ndiponso amene anakuumba,
Amene wakhala akukuthandiza kuyambira uli mʼmimba,* wanena kuti:
4 Iwo adzaphuka ngati udzu wobiriwira,+
Ndiponso ngati mitengo ya msondodzi mʼmphepete mwa mitsinje yamadzi.
5 Munthu adzati: “Ine ndine wa Yehova.”+
Wina adzadzipatsa dzina la Yakobo,
Winanso adzalemba padzanja lake kuti: “Ndine wa Yehova.”
Ndipo adzatenga dzina la Isiraeli.’
‘Ine ndine woyamba ndi womaliza.+
Ndipo palibenso Mulungu wina kupatulapo ine.+
7 Kodi ndi ndani amene angafanane ndi ine?+
Ayankhe molimba mtima ndi kupereka umboni wake kwa ine.+
Kuyambira nthawi imene ndinakhazikitsa anthu akalekale,
Iwo anene zinthu zimene zichitike posachedwapa
Ndi zimene zidzachitike mʼtsogolo.
Kodi sindinauziretu aliyense wa inu ndi kulengeza zimenezi?
Inu ndinu mboni zanga.+
Kodi palinso Mulungu wina kupatulapo ine?
Ayi, palibe Thanthwe lina.+ Palibe lina limene ndikulidziwa.’”
9 Anthu onse opanga zifaniziro zosema ndi opanda pake,
Ndipo mafano awo amene amawanyadira ndi opanda phindu.+
Mofanana ndi mboni zawo, mafanowo saona chilichonse ndipo sadziwa chilichonse,+
Choncho anthu amene anawapanga adzachititsidwa manyazi.+
10 Kodi pali aliyense wopusa amene angafike popanga mulungu kapena fano lopangidwa ndi chitsulo chosungunula,*
Lomwe ndi lopanda phindu?+
11 Anzake onse adzachititsidwa manyazi,+
Amisiriwo ndi anthu basi.
Onsewo asonkhane pamodzi ndipo akhale pamalo awo.
Adzachita mantha ndipo onsewo adzachititsidwa manyazi.
12 Munthu wosula zitsulo akugwiritsa ntchito chida chake posula chitsulo chimene wachiwotcha pamoto wamakala.
Akuchiwongola ndi hamala,
Akuchisula ndi dzanja lake lamphamvu.+
Kenako wamva njala ndipo mphamvu zake zatha.
Sanamwe madzi ndipo watopa.
13 Mmisiri wosema mtengo watambasula chingwe choyezera. Walemba mtengowo ndi choko chofiira.
Wausema ndi sompho* ndipo waulemberera ndi chipangizo cholembera mizere yozungulira.
14 Pali munthu amene ntchito yake ndi yogwetsa mitengo ya mkungudza.
Iye amasankha mtengo wamtundu winawake, mtengo waukulu kwambiri,
Ndipo amausiya kuti ukule nʼkukhwima pakati pa mitengo yamʼnkhalango.+
Iye amadzala mtengo wa paini ndipo mvula imaukulitsa.
15 Kenako mtengowo umakhala nkhuni zoti munthu akolezere moto.
Amatenga mbali ina ya mtengowo kuti asonkhere moto woti aziwotha.
Amayatsa moto nʼkuphikapo mkate.
Koma amasemanso mulungu nʼkumamulambira.
Mtengowo amaupanga chifaniziro chosema ndipo amachigwadira.+
16 Hafu ya mtengowo waiwotcha pamoto.
Mtengo umene wauwotcha pamotowo wawotchera nyama imene wadya ndipo wakhuta.
Wawothanso moto wake ndipo wanena kuti:
“Eya! Ndamva kutenthera. Ndaona kuwala kwa moto.”
17 Koma mtengo wotsalawo wapangira mulungu, wapangira chifaniziro chake chosema.
Akuchiweramira komanso kuchilambira.
Akupemphera kwa chifanizirocho kuti:
“Ndipulumutseni, chifukwa ndinu mulungu wanga.”+
18 Iwo sadziwa kanthu ndipo palibe chimene amamvetsa,+
Chifukwa maso awo ndi otseka ndipo sangaone,
Ndipo mitima yawo sizindikira zinthu.
19 Palibe amene amaganiza mumtima mwake
Kapena amene akudziwa zinthu, kapenanso amene amamvetsa zinthu kuti adzifunse kuti:
“Hafu ya mtengowu ndasonkhera moto,
Ndipo pamakala ake ndaphikapo mkate komanso ndawotcha nyama nʼkudya.
Ndiye kodi wotsalawu ndipangire chinthu chonyansa?+
Kodi zoona ndilambire chinthu chopangidwa ndi mtengo?”*
20 Iye akudya phulusa.
Mtima wake umene wapusitsidwa wamusocheretsa.
Iye sangathe kudzipulumutsa kapena kunena kuti:
“Kodi chinthu chimene chili mʼdzanja langa lamanjachi si chabodza?”
21 “Kumbukira zinthu zimenezi iwe Yakobo ndiponso iwe Isiraeli,
Chifukwa ndiwe mtumiki wanga.
Ine ndinakupanga ndipo iweyo ndiwe mtumiki wanga.+
Iwe Isiraeli, ine sindidzakuiwala.+
22 Ndidzafafaniza zolakwa zako ndipo zidzakhala ngati ndaziphimba ndi mtambo+
Ndipo machimo ako adzakhala ngati ndawaphimba ndi mtambo waukulu.
Bwerera kwa ine, ndipo ine ndidzakuwombola.+
23 Fuulani mosangalala kumwamba inu,
Chifukwa Yehova wachita zimenezi.
Fuulani posonyeza kupambana, inu malo otsika kwambiri a dziko lapansi.
Mapiri inu, fuulani mosangalala,+
Iwe nkhalango ndi inu mitengo yonse imene ili mmenemo,
Chifukwa Yehova wawombola Yakobo,
Ndipo wasonyeza kukongola kwake pa Isiraeli.”+
“Ine ndine Yehova amene ndinapanga chilichonse.
Kodi ndi ndani amene anali ndi ine?
25 Ndimalepheretsa zizindikiro za anthu olankhula zinthu zopanda pake,*
Ndipo ndine amene ndimachititsa olosera kuti azichita zinthu ngati anthu opusa.+
Ndine amene ndimasokoneza anthu anzeru
Ndiponso amene ndimachititsa kuti nzeru zawo zikhale zopusa.+
26 Ndine amene ndimachititsa mawu a mtumiki wanga kuti akwaniritsidwe
Ndiponso amene ndimakwaniritsa mawu onse amene amithenga anga analosera.+
Ndine amene ndikunena za Yerusalemu kuti, ‘Muzidzakhala anthu.’+
Ndikunenanso za mizinda ya ku Yuda kuti, ‘Idzamangidwanso,+
Ndipo ndidzakonza malo ake amene anawonongedwa.’+
27 Ndine amene ndikuuza madzi akuya kuti, ‘Iphwa
Ndipo mitsinje yako yonse ndidzaiumitsa.’+
28 Ndine amene ndikunena za Koresi+ kuti, ‘Iye ndi mʼbusa wanga,
Ndipo adzakwaniritsa bwinobwino zonse zimene ndikufuna,’+
Amene ndanena zokhudza Yerusalemu kuti, ‘Adzamangidwanso,’
Ndiponso zokhudza kachisi kuti, ‘Maziko ako adzamangidwa.’”+
45 Izi ndi zimene Yehova akunena kwa wodzozedwa wake, kwa Koresi,+
Amene wamugwira dzanja lake lamanja+
Kuti agonjetse mitundu ya anthu pamaso pake,+
Kuti alande zida zankhondo za mafumu,*
Kuti amutsegulire zitseko zokhala ziwiriziwiri,
Kuti mageti adzakhale osatseka. Iye wamuuza kuti:
3 Ndidzakupatsa chuma chimene chili mumdima
Ndiponso chuma chimene chabisidwa mʼmalo achinsinsi,+
Kuti udziwe kuti ine ndine Yehova,
Mulungu wa Isiraeli, amene ndikukuitana pokutchula dzina lako.+
4 Chifukwa cha mtumiki wanga Yakobo ndi Isiraeli wosankhidwa wanga,
Ine ndikukuitana pokutchula dzina lako.
Ndikukupatsa dzina laulemu, ngakhale kuti sukundidziwa.
5 Ine ndine Yehova ndipo palibenso wina.
Palibenso Mulungu wina kupatulapo ine.+
Ndidzakupatsa mphamvu* ngakhale kuti sukundidziwa,
6 Kuti anthu adziwe
Kuyambira kumene kumatulukira dzuwa mpaka kumene limalowera*
Kuti palibenso wina kupatulapo ine.+
Ine ndine Yehova ndipo palibenso wina.+
7 Ndimapanga kuwala+ ndiponso ndimabweretsa mdima.+
Ndimabweretsa mtendere+ komanso tsoka.+
Ine Yehova ndimapanga zonsezi.
Dziko lapansi litseguke ndipo libale chipulumutso,
Pa nthawi imodzimodziyo lichititse kuti chilungamo chiphuke.+
Ine Yehova ndachititsa zimenezi.”
9 Tsoka kwa amene akulimbana* ndi amene anamupanga,
Chifukwa iye ali ngati phale
Limene lili pakati pa mapale ena amene ali pansi.
Kodi dongo lingafunse woumba mbiya* kuti: “Kodi ukupanga chiyani?”+
Kapena kodi chinthu chimene unapanga chinganene kuti: “Amene uja alibe manja”?*
10 Tsoka kwa amene akufunsa bambo kuti: “Kodi nʼchiyani mwaberekachi?”
Ndiponso wofunsa mkazi kuti: “Kodi nʼchiyani mukuberekachi?”*
11 Yehova, Woyera wa Isiraeli+ ndiponso amene anamuumba, wanena kuti:
“Kodi ukukaikira mawu anga okhudza zinthu zimene zikubwera
Ndipo ukundilamula zinthu zokhudza ana anga+ komanso ntchito ya manja anga?
12 Ineyo ndinapanga dziko lapansi+ ndipo ndinalenga munthu nʼkumuika padzikolo.+
Ndinatambasula kumwamba ndi manja angawa,+
Ndipo zinthu zonse zimene zili kumwambako* ndimazipatsa malamulo.+
13 Ine ndapatsa munthu mphamvu kuti achitepo kanthu mwachilungamo,+
Ndipo njira zake zonse ndidzaziwongola.
Iye ndi amene adzamange mzinda wanga+
Komanso kumasula anthu anga amene ali ku ukapolo,+ popanda malipiro kapena chiphuphu,”+ akutero Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.
14 Yehova wanena kuti:
“Phindu la ku Iguputo,* malonda* a ku Itiyopiya ndi Asabeya, anthu ataliatali,
Adzabwera kwa iwe ndipo adzakhala ako.
Iwo adzayenda pambuyo pako atamangidwa mʼmaunyolo
Adzabwera nʼkudzakugwadira.+
Adzapemphera kwa iwe kuti, ‘Zoonadi Mulungu ali ndi iwe,+
Ndipo palibenso wina. Palibenso Mulungu wina.’”
16 Anthu onse adzachititsidwa manyazi ndipo adzanyozeka.
Anthu onse amene amapanga mafano adzachoka mwamanyazi.+
17 Koma Isiraeli adzapulumutsidwa ndi Yehova ndipo chipulumutso chake chidzakhala chosatha.+
Inu simudzachititsidwa manyazi kapena kunyozeka mpaka kalekale.+
18 Chifukwa Yehova,
Mlengi wakumwamba,+ Mulungu woona,
Amene anaumba dziko lapansi, amene analipanga ndi kulikhazikitsa mwamphamvu,+
Amene sanalilenge popanda cholinga,* koma analiumba kuti anthu akhalemo,+ wanena kuti:
“Ine ndine Yehova ndipo palibenso wina.
19 Ine sindinalankhule mʼmalo obisika,+ mʼdziko lamdima.
Sindinauze mbadwa* za Yakobo kuti,
‘Muzindifunafuna pachabe.’
Ine ndine Yehova, amene ndimalankhula zolungama komanso kulengeza zinthu zimene ndi zolondola.+
20 Sonkhanani pamodzi ndipo mubwere.
Mubwere pamodzi, inu anthu amene mwapulumuka ku mitundu ya anthu.+
Amene amanyamula zifaniziro zawo zogoba sadziwa chilichonse
Ndipo amapemphera kwa mulungu woti sangawapulumutse.+
21 Lankhulani ndipo mufotokoze mlandu wanu.
Mukambirane mogwirizana.
Kodi ndi ndani ananeneratu zimenezi kalekale
Nʼkuzilengeza kuyambira kalekale?
Kodi si ine, Yehova?
Palibenso Mulungu wina koma ine ndekha.
Ine ndi Mulungu wolungama komanso Mpulumutsi+ ndipo palibenso wina kupatulapo ine.+
22 Tembenukirani kwa ine kuti mupulumuke,+ inu nonse amene muli kumalekezero a dziko lapansi,
Chifukwa ine ndine Mulungu ndipo palibenso wina.+
23 Ndalumbira pa dzina langa.
Mawu amene atuluka pakamwa panga ndi olondola,
Ndipo adzakwaniritsidwa ndithu:+
Bondo lililonse lidzandigwadira,
Ndipo lilime lililonse lidzalumbira kuti lidzakhala lokhulupirika kwa ine,+
24 Nʼkunena kuti, ‘Zoonadi, kwa Yehova kuli chilungamo chechicheni komanso mphamvu.
Onse omukwiyira adzabwera kwa iye mwamanyazi.
25 Mbadwa* zonse za Isiraeli zidzaona kuti zinachita bwino kutumikira Yehova,+
Ndipo zidzadzitama chifukwa cha zinthu zimene iye anazichitira.’”
46 Beli wawerama+ ndipo Nebo wagwada.
Mafano awo anyamulidwa ndi nyama, nyama zonyamula katundu.+
Mafanowo ali ngati katundu wolemera kwa nyama zotopa.
2 Milungu imeneyi imawerama komanso kugwada pa nthawi imodzi.
Singapulumutse katunduyo,*
Ndipo nayonso imatengedwa kupita ku ukapolo.
3 “Inu anyumba ya Yakobo ndimvetsereni, komanso inu nonse otsala a mʼnyumba ya Isiraeli,+
Inu amene ndakuthandizani kuyambira pamene munabadwa ndiponso kukunyamulani kuyambira pamene munatuluka mʼmimba.+
4 Ngakhale mudzakalambe, ine ndidzakhala chimodzimodzi.+
Ngakhale tsitsi lanu lidzachite imvi, ine ndidzapitiriza kukunyamulani.
Ndidzakunyamulani, kukuthandizani komanso kukupulumutsani ngati mmene ndakhala ndikuchitira.+
5 Kodi mungandifananitse kapena kundiyerekezera ndi ndani?+
Kodi munganene kuti ndine wofanana ndi ndani?+
6 Pali anthu amene amakhuthula golide mʼzikwama zawo.
Amayeza siliva pasikelo.
Iwo amalemba ganyu mmisiri wa zitsulo ndipo amapanga mulungu ndi zinthu zimenezi.+
Kenako anthuwo amayamba kumuweramira ndi kumulambira.*+
7 Iwo amamunyamula pamapewa awo.+
Amamutenga nʼkukamuika pamalo ake ndipo mulunguyo amangoima pomwepo.
Sasuntha pamene amuikapo.+
Anthuwo amamuitana mofuula, koma sayankha.
Sangapulumutse munthu amene ali pamavuto.+
8 Kumbukirani zimenezi ndipo mulimbe mtima.
Muziganizire mumtima mwanu, anthu ochimwa inu.
9 Kumbukirani zinthu zoyambirira zimene zinachitika kalekale,
Kuti ine ndine Mulungu ndipo palibenso wina.
Ine ndine Mulungu ndipo palibe aliyense wofanana ndi ine.+
10 Kutatsala nthawi yaitali, ndimaneneratu zimene zidzachitike,
Ndipo kale kwambiri ndinaneneratu zinthu zimene zidzachitike mʼtsogolo.+
Ine ndimanena kuti, ‘Zolinga zanga zidzachitikadi,+
Ndipo ndidzachita chilichonse chimene ndikufuna.’+
11 Ine ndikuitana mbalame yodya nyama kuchokera kotulukira dzuwa,*+
Ndikuitana munthu kuchokera kudziko lakutali kuti adzachite zolinga zanga.+
Ineyo ndalankhula ndipo ndidzazichita.
Ndakonza kuti zimenezi zichitike komanso ndidzazichita.+
13 Ine ndabweretsa pafupi chilungamo changa.
Chilungamocho sichili kutali,
Ndipo chipulumutso changa sichidzachedwa.+
Ndidzapereka chipulumutso mu Ziyoni, ndipo Isiraeli ndidzamʼpatsa ulemerero wanga.”+
Ukhale padothi pomwe palibe mpando wachifumu,+
Iwe mwana wamkazi wa Akasidi,
Chifukwa anthu sadzakutchulanso kuti ndiwe wolekereredwa ndiponso wosasatitsidwa.
2 Tenga mphero upere ufa.
Vula nsalu yako yophimba kumutu.
Vula chovala chako ndipo miyendo yako ionekere.
Uwoloke mitsinje.
3 Anthu adzaona maliseche ako.
Manyazi ako adzaonekera.
Ine ndidzabwezera+ ndipo palibe amene adzanditsekereze.*
4 “Amene akutiwombola
Dzina lake ndi Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.
Iye ndi Woyera wa Isiraeli.”+
6 Ine ndinakwiyira anthu anga.+
Koma iwe sunawachitire chifundo.+
Ngakhale munthu wokalamba unamusenzetsa goli lolemera kwambiri.+
7 Iwe unanena kuti: “Nthawi zonse ine ndidzakhala Dona* mpaka kalekale.”+
Sunaganizire zinthu zimenezi mumtima mwako.
Sunaganizire kuti zidzatha bwanji.
8 Tsopano imva izi, iwe amene umakonda zosangalatsa,+
Amene umakhala motetezeka, iwe amene umanena mumtima mwako kuti:
“Ndine ndekha, palibenso wina.+
Sindidzakhala wamasiye
Ndipo ana anga sadzafa.”+
9 Koma zinthu ziwiri izi zidzakugwera modzidzimutsa tsiku limodzi:+
Ana ako adzafa ndiponso udzakhala wamasiye.
Zinthu zonsezi zidzakugwera ndithu,+
Chifukwa* wachita zanyanga zochuluka komanso chifukwa cha zamatsenga zako zonse zamphamvu.+
10 Iwe unkadalira zoipa zimene unkachita.
Unkanena kuti: “Palibe amene akundiona.”
Nzeru zako komanso kudziwa zinthu ndi zimene zinakusocheretsa,
Ndipo mumtima mwako umanena kuti: “Ndine ndekha, palibenso wina.”
Mavuto adzakugwera ndipo sudzatha kuwapewa.
Chiwonongeko chimene sunkachiyembekezera chidzakupeza modzidzimutsa.+
12 Choncho pitiriza kuchita zanyanga komanso zamatsenga zako zambirimbirizo,+
Zimene wazivutikira kuyambira uli mwana.
Mwina zingakuthandize,
Mwina zichititsa kuti anthu achite mantha.
13 Alangizi ako ambirimbiri akutopetsa.
Anthu amene amalambira zinthu zakumwamba,* amene amayangʼanitsitsa nyenyezi,+
Amene amakudziwitsa zimene zikuchitikire
Mwezi watsopano ukaoneka,
Auze abwere adzakupulumutse.
14 Iwotu ali ngati mapesi.
Moto udzawawotcha.
Sangathe kudzipulumutsa ku mphamvu ya moto walawilawi.
Moto umenewu suli ngati moto wamakala woti anthu nʼkumawotha,
Si moto woti anthu nʼkuuyandikira.
15 Umu ndi mmene amatsenga ako adzakhalire
Amene wakhala ukuvutikira nawo limodzi kuyambira uli mwana.
Iwo adzabalalika, aliyense kulowera njira yake*
Ndipo sipadzakhala aliyense woti akupulumutse.+
48 Imvani izi, inu a mʼnyumba ya Yakobo,
Inu amene mumadzitchula dzina la Isiraeli+
Ndiponso amene munatuluka kuchokera mʼmadzi a Yuda,*
Inu amene mumalumbira pa dzina la Yehova+
Ndiponso amene mumapemphera kwa Mulungu wa Isiraeli,
Ngakhale kuti simuchita zimenezi kuchokera pansi pa mtima ndipo simuchita zoyenera.+
2 Chifukwa mumanena kuti ndinu anthu amumzinda woyera+
Ndipo mumadalira Mulungu wa Isiraeli+
Amene dzina lake ndi Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.
3 “Ndinakuuziranitu kalekale zinthu zimene zidzachitike.
Zinatuluka pakamwa panga,
Ndipo ndinazichititsa kuti zidziwike.+
Mwadzidzidzi, ndinachita zimene ndinanena ndipo zinachitikadi.+
4 Chifukwa ndinadziwa kuti ndinu anthu ouma khosi,
Kuti khosi lanu lili ngati mtsempha wachitsulo ndiponso kuti chipumi chanu chili ngati kopa,*+
5 Ine ndinakuuzani kalekale.
Zisanachitike nʼkomwe, ine ndinachititsa kuti muzimve,
Kuti musanene kuti, ‘Fano langa ndi limene linachita zimenezi.
Chifaniziro changa chosema komanso chifaniziro chachitsulo* nʼzimene zinalamula zimenezi.’
6 Inuyo mwamva komanso kuona zonsezo.
Kodi simudzauza ena zimenezi?+
Kuyambira panopa kupita mʼtsogolo, ndikulengeza zinthu zatsopano kwa inu,+
Zinsinsi zobisika zimene simunkazidziwa.
7 Zinthu zimenezi zikulengedwa panopa osati kalekale,
Zinthu zimene simunazimvepo mʼmbuyomu.
Choncho simunganene kuti, ‘Ifetu tinkazidziwa kale zimenezi.’
Chifukwa ndikudziwa kuti inu ndi achinyengo,+
Ndipo kuyambira pamene munabadwa mumatchedwa wochimwa.+
9 Koma ndidzabweza mkwiyo wanga chifukwa cha dzina langa.+
Chifukwa cha ulemerero wanga, ine ndidzadziletsa
Ndipo sindidzakuwonongani.+
10 Taonani! Ndinakuyengani koma osati ngati mmene amayengera siliva.+
Ndinakuyesani* mʼngʼanjo ya mavuto.+
11 Ndithu, ndidzachitapo kanthu chifukwa cha dzina langa,+
Chifukwa sindingalole kuti dzina langa liipitsidwe.+
Sindipereka ulemerero wanga kwa wina aliyense.*
12 Ndimvere iwe Yakobo, iwe Isiraeli amene ndinakuitana.
Ine sindinasinthe.+ Ine ndine woyamba. Ndinenso womaliza.+
13 Dzanja langa linayala maziko a dziko lapansi,+
Ndipo dzanja langa lamanja linatambasula kumwamba.+
Ndikaitana zinthu zimenezi, zimaimirira limodzi.
14 Sonkhanani pamodzi nonsenu ndipo mumvetsere.
Ndi ndani pakati pawo amene walengeza zinthu zimenezi?
Yehova wamukonda.+
15 Ineyo ndalankhula, komanso ndamuitana.+
Ndamubweretsa, ndipo zochita zake zidzamuyendera bwino.+
16 Bwerani pafupi ndi ine ndipo mumve izi.
Kuyambira pachiyambi, ine sindinalankhulirepo mʼmalo obisika.+
Kuyambira pamene zinachitika ine ndinalipo.”
Ndipo panopa Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, watumiza ine komanso* mzimu wake.
17 Yehova, Wokuwombolani, Woyera wa Isiraeli,+ wanena kuti:
“Ine Yehova ndine Mulungu wanu,
Amene ndimakuphunzitsani kuti zinthu zikuyendereni bwino,*+
Amene ndimakutsogolerani mʼnjira imene mukuyenera kuyenda.+
18 Zingakhale bwino kwambiri mutamvera malamulo anga!+
Mukatero mtendere wanu udzakhala ngati mtsinje+
Ndipo chilungamo chanu chidzakhala ngati mafunde a mʼnyanja.+
Dzina lawo silidzachotsedwa kapena kuwonongedwa pamaso panga.”
Thawani mʼmanja mwa Akasidi.
Lengezani zimenezi mofuula komanso mosangalala. Uzani anthu zimenezi.+
Zineneni kuti anthu azidziwe mpaka kumalekezero a dziko lapansi.+
Munene kuti: “Yehova wawombola mtumiki wake Yakobo.+
21 Iwo sanamve ludzu pamene iye ankawatsogolera kudutsa mʼchipululu.+
Iye anachititsa kuti madzi atuluke pathanthwe kuti iwo amwe.
Anangʼamba thanthwe nʼkupangitsa kuti madzi atuluke.”+
22 Yehova wanena kuti, “Oipa alibe mtendere.”+
Yehova anandiitana ndisanabadwe.*+
Kuyambira nthawi imene ndinali mʼmimba mwa mayi anga, anatchula dzina langa.
2 Iye anachititsa kuti mʼkamwa mwanga mukhale ngati lupanga lakuthwa.
Wandibisa mumthunzi wa dzanja lake.+
Anandisandutsa muvi wonola bwino.
Anandibisa mʼkachikwama kake koikamo mivi.
3 Anandiuza kuti: “Iwe Isiraeli ndiwe mtumiki wanga.+
Kudzera mwa iwe ndidzaonetsa ulemerero wanga.”+
4 Koma ine ndinati: “Ndangovutika pachabe.
Mphamvu zanga zangopita pachabe, pa zinthu zopanda pake.
5 Ndiyeno Yehova amene anandipanga ndili mʼmimba kuti ndikhale mtumiki wake,
Wandiuza kuti nditenge Yakobo nʼkumubwezera kwa iye,
Nʼcholinga choti Isiraeli asonkhanitsidwe kwa iye.+
Ine ndidzalemekezedwa pamaso pa Yehova
Ndipo Mulungu wanga adzakhala mphamvu yanga.
6 Ndiyeno iye anati: “Sikuti wangokhala mtumiki wanga
Kuti ubwezeretse mafuko a Yakobo
Ndiponso kuti Aisiraeli amene ali otetezeka uwabwezere kwawo.
Koma ndakuperekanso kuti ukhale kuwala kwa anthu a mitundu ina,+
Kuti chipulumutso changa chifike kumalekezero a dziko lapansi.”+
7 Yehova, Wowombola Isiraeli, Woyera wake,+ wauza amene amanyozedwa kwambiri,+ amene mtundu wa anthu umadana naye, mtumiki wa olamulira kuti:
“Mafumu adzaona nʼkuimirira,
Ndipo akalonga adzagwada pansi
Chifukwa cha Yehova yemwe ndi wokhulupirika,+
Woyera wa Isiraeli, amene wakusankha.”+
8 Yehova wanena kuti:
“Pa nthawi yosonyeza kukoma mtima kwanga, ndinakuyankha.+
Ndipo pa tsiku la chipulumutso ndinakuthandiza.+
Ndinkakuteteza kuti ndikupereke ngati pangano kwa anthu,+
Kuti ndikonzenso dzikolo,
Kuti anthuwo atengenso cholowa chawo chimene chinali bwinja,+
Ndiponso amene ali mumdima+ kuti, ‘Bwerani poyera kuti anthu akuoneni!’
Iwo adzadya msipu mʼmphepete mwa msewu,
Ndipo mʼmphepete mwa njira zonse zimene zimadutsidwadutsidwa* mudzakhala malo awo odyeramo msipu.
10 Iwo sadzakhala ndi njala ndipo sadzamva ludzu,+
Komanso sadzamva kutentha kapena kupsa ndi dzuwa.+
Chifukwa amene amawachitira chifundo adzawatsogolera+
Ndipo adzapita nawo kumene kuli akasupe amadzi.+
11 Ndidzachititsa kuti mapiri anga onse akhale njira,
Ndipo misewu yanga yonse idzakhala pamalo okwera.+
12 Taonani! Anthu akuchokera kutali,+
Ena akuchokera kumpoto ndi kumadzulo.
Komanso ena akuchokera kudziko la Sinimu.”+
13 Fuulani mosangalala kumwamba inu ndipo sangalala iwe dziko lapansi.+
Mapiri asangalale ndipo afuule mosangalala.+
14 Koma Ziyoni ankangonena kuti:
“Yehova wandisiya+ ndipo Yehova wandiiwala.”+
15 Kodi mayi angaiwale mwana wake woyamwa
Kapena kulephera kuchitira chifundo mwana wochokera mʼmimba mwake?
Ngakhale amayi amenewa ataiwala, ine sindingakuiwale.+
16 Taona! Ndalemba dzina lako mʼmanja mwanga.
Makoma ako ali pamaso panga nthawi zonse.
17 Ana ako abwerera mofulumira.
Anthu amene anakugwetsa nʼkukuwononga adzachoka kwa iwe.
18 Kweza maso ako uone zonse zimene zikuchitika mokuzungulira.
Onse akusonkhana pamodzi.+
Akubwera kwa iwe.
Yehova wanena kuti: “Pali ine Mulungu wamoyo,
Onsewo udzadzikongoletsa nawo ngati zokongoletsera,
Ndipo udzawavala ngati ndiwe mkwatibwi.
19 Ngakhale kuti malo ako anawonongedwa komanso kusakazidwa ndipo dziko lako linali mabwinja,+
Tsopano anthu amene adzakhale mmenemo malo adzawachepera moti adzakhala mopanikizana,+
20 Ana ako amene unabereka ana ena onse atamwalira, adzakuuza kuti,
‘Malowa atichepera.
Tipezereni malo oti tizikhalamo.’+
21 Ndipo mumtima mwako udzanena kuti,
‘Kodi bambo amene wandiberekera anawa ndi ndani,
Popeza ine ndine mayi woferedwa ana ndiponso amene anasiya kubereka,
Mayi amene anatengedwa kupita kudziko lina kuti akakhale mkaidi?
Ndi ndani amene walera ana amenewa?+
22 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti:
“Taona! Ineyo ndidzakwezera dzanja langa mitundu ya anthu,
Ndipo anthu a mitundu ina ndidzawakwezera chizindikiro.+
Iwo adzakubweretsera ana ako aamuna atawanyamula mʼmanja,*
Ndipo ana ako aakazi adzawanyamula paphewa.+
Iwo adzakugwadira mpaka nkhope zawo pansi+
Ndipo adzanyambita fumbi lakumapazi ako.+
Choncho iwe udzadziwa kuti ine ndine Yehova.
Anthu amene amandikhulupirira sadzachita manyazi.”+
24 Kodi anthu amene agwidwa kale angalandidwe mʼmanja mwa munthu wamphamvu,
Kapena kodi anthu amene agwidwa ndi wolamulira wankhanza angapulumutsidwe?
25 Koma Yehova akunena kuti:
“Ngakhale anthu amene agwidwa ndi munthu wamphamvu adzalandidwa,+
Ndipo amene anagwidwa ndi wolamulira wankhanza adzapulumutsidwa.+
Ndidzalimbana ndi aliyense amene akulimbana nawe,+
Ndipo ana ako ndidzawapulumutsa.
26 Amene akukuzunza ndidzawachititsa kuti adye mnofu wawo womwe,
Ndipo adzaledzera ndi magazi awo omwe ngati kuti amwa vinyo wotsekemera.
Anthu onse adzadziwa kuti ine ndine Yehova,+
Mpulumutsi wako+ ndiponso Wokuwombola,+
Mulungu Wamphamvu wa Yakobo.”+
50 Yehova wanena kuti:
“Kodi kalata yothetsera ukwati+ wa mayi anu amene ndinawathamangitsa ili kuti?
Kapena kodi ndakugulitsani kwa munthu uti amene ndinali naye ngongole?
Inutu munagulitsidwa chifukwa cha zolakwa zanu,+
Ndipo mayi anu anathamangitsidwa chifukwa cha machimo anu.+
2 Ndiye nʼchifukwa chiyani nditabwera sindinapeze aliyense?
Nʼchifukwa chiyani nditaitana palibe amene anayankha?+
Kodi dzanja langa lafupika kwambiri moti silingathe kuwombola,
Kapena kodi ine ndilibe mphamvu zopulumutsira?+
Nsomba zake zimawola chifukwa chakuti mulibe madzi
Ndipo zimafa chifukwa cha ludzu.
4 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wandipatsa lilime la anthu ophunzitsidwa bwino*+
Kuti ndidziwe mmene ndingayankhire* munthu amene watopa, ndi mawu oyenera.+
Sindinatembenukire kwina.+
6 Msana wanga ndinaupereka kwa anthu amene ankandimenya
Ndipo masaya anga ndinawapereka kwa anthu amene ankandizula ndevu.
Sindinabise nkhope yanga kuti asaichitire zinthu zochititsa manyazi komanso kuti asailavulire.+
7 Koma Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, adzandithandiza.+
Nʼchifukwa chake sindidzamva kuti ndanyozeka.
Nʼchifukwa chake ndalimbitsa nkhope yanga ngati mwala wa nsangalabwi,+
Ndipo ndikudziwa kuti sindidzachititsidwa manyazi.
8 Amene amanena kuti ndine wolungama ali pafupi.
Ndi ndani angandiimbe* mlandu?+
Tiyeni tikaonane pabwalo lamilandu.
Kodi ndi ndani amene akufuna kundiimba mlandu?
Abwere pafupi ndi ine.
9 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, adzandithandiza.
Ndi ndani amene adzanene kuti ndine wolakwa?
Onse adzatha ngati chovala.
Njenjete* idzawadya.
Ndi ndani amene amayenda mumdima wandiweyani, popanda kuwala kulikonse?
Iye akhulupirire dzina la Yehova ndipo adalire Mulungu wake.
11 “Inu nonse amene mukuyatsa moto,
Amene mukuchititsa kuti uzithetheka,
Yendani mʼkuwala kwa moto wanuwo,
Pakati pa moto umene ukuthethekawo.
Izi ndi zimene mudzalandire kuchokera mʼdzanja langa:
Mudzagona pansi mukumva ululu woopsa.”
51 “Ndimvereni, inu anthu amene mukufunafuna chilungamo,
Inu amene mukufunafuna Yehova.
Yangʼanani kuthanthwe limene munasemedwako,
Ndi pamalo okumbapo miyala pamene munakumbidwa.
Chifukwa Abulahamu anali munthu mmodzi pamene ndinamuitana,+
Koma ndinamudalitsa ndi kuchulukitsa mbadwa zake.+
3 Chifukwa Yehova adzatonthoza Ziyoni.+
Iye adzatonthoza malo ake onse amene anawonongedwa.+
Adzachititsa chipululu chake kukhala ngati Edeni+
Ndipo dera lake lachipululu lidzakhala ngati munda wa Yehova.+
Mwa iye mudzakhala kusangalala ndi kukondwera,
Kuyamikira ndi kuimba nyimbo zosangalatsa.+
Chifukwa kwa ine kudzachokera lamulo+
Ndipo ndidzachititsa kuti chilungamo changa chikhazikike ngati kuwala ku mitundu ya anthu.+
5 Chilungamo changa chayandikira.+
6 Kwezani maso anu kumwamba,
Ndipo yangʼanani padziko lapansi.
Kumwamba kudzabenthukabenthuka nʼkumwazika ngati utsi,
Dziko lapansi lidzatha ngati chovala,
Ndipo anthu amene akukhala mmenemo adzafa ngati ntchentche.
7 Ndimvereni, inu anthu amene mumadziwa chilungamo,
Musachite mantha ndi mawu otonza amene anthu akunena
Ndipo musaope chifukwa cha mawu awo onyoza.
Koma chilungamo changa chidzakhala mpaka kalekale
Ndipo chipulumutso changa chidzafikira mibadwo yonse.”+
Dzuka ngati masiku akale, ngati mʼmibadwo yakale.
10 Kodi si iwe amene unaumitsa nyanja, amene unaumitsa madzi akuya kwambiri?+
Si iwe kodi amene unapangitsa kuti pansi pa nyanja pakhale njira yoti anthu owomboledwa awolokerepo?+
11 Anthu owomboledwa a Yehova adzabwerera.+
Adzabwera ku Ziyoni akufuula mosangalala,+
Ndipo pamutu pawo padzakhala chisangalalo mpaka kalekale.+
Iwo adzapeza chisangalalo ndi chimwemwe,
Ndipo chisoni komanso kulira zidzachoka.+
12 “Ineyo ndi amene ndikukutonthoza.+
Ndiye nʼchifukwa chiyani ukuopa munthu woti adzafa+
Ndiponso mwana wa munthu amene adzanyale ngati udzu wobiriwira?
13 Nʼchifukwa chiyani ukuiwala Yehova amene anakupanga,+
Amene anatambasula kumwamba+ ndi kuyala maziko a dziko lapansi?
Ndipo tsiku lonse unkangokhalira kuopa mkwiyo wa amene amakupondereza,
Ngati kuti ali ndi mphamvu zoti akanatha kukuwononga.
Kodi tsopano mkwiyo wa amene ankakupondereza uja uli kuti?
14 Yemwe wawerama atamangidwa maunyolo amasulidwa posachedwapa.+
Iye sadzafa nʼkutsikira kudzenje,
Komanso sadzasowa chakudya.
15 Koma ine ndine Yehova Mulungu wako,
Amene ndimavundula nyanja nʼkupangitsa kuti mafunde ake achite phokoso+
Dzina langa ndine Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.+
16 Ndidzaika mawu anga mʼkamwa mwako,
Ndipo ndidzakuphimba ndi mthunzi wa dzanja langa,+
Kuti ndikhazikitse kumwamba komanso kuyala maziko a dziko lapansi+
Ndiponso kuti ndiuze Ziyoni kuti, ‘Ndinu anthu anga.’+
17 Dzuka! Dzuka! Imirira iwe Yerusalemu,+
Iwe amene wamwa zinthu zamʼkapu ya mkwiyo wa Yehova kuchokera mʼdzanja lake.
Iweyo wamwa zimene zili mʼchipanda,
Wagugudiza kapu yochititsa kuti munthu aziyenda dzandidzandi.+
18 Pa ana onse amene iye anabereka, palibe ndi mmodzi yemwe woti amutsogolere,
Ndipo pa ana onse amene iye analera, palibe ndi mmodzi yemwe amene wagwira dzanja lake.
19 Zinthu ziwiri izi zakugwera.
Ndi ndani amene akumvere chisoni?
Kuwonongedwa ndi kusakazidwa, njala ndi lupanga!+
Kodi ndi ndani amene akutonthoze?+
Agona pamphambano za misewu yonse
Ngati nkhosa zamʼtchire zimene zakodwa mu ukonde.
Iwo akhuta mkwiyo wa Yehova, akhuta kudzudzula kwa Mulungu wako.”
21 Choncho mvetsera izi,
Iwe mkazi wovutika ndiponso woledzera, koma osati ndi vinyo.
22 Ambuye wako Yehova, Mulungu wako, amene amateteza anthu ake, wanena kuti:
“Taona! Ine ndidzachotsa mʼmanja mwako kapu yochititsa munthu kudzandira,+
Chipanda kapena kuti kapu ya mkwiyo wanga.
Sudzamwanso zinthu zamʼkapu imeneyi.+
23 Ndidzaika kapu imeneyi mʼmanja mwa amene akukuvutitsa,+
Amene amakuuza kuti, ‘Werama kuti tiyende pamsana pako.’
Choncho unachititsa kuti msana wako ukhale ngati malo oti azipondapo,
Ngati msewu woti azidutsamo.”
52 Dzuka! Dzuka! Vala mphamvu+ iwe Ziyoni.+
Vala zovala zako zokongola+ iwe Yerusalemu, mzinda woyera.
Chifukwa munthu wosadulidwa ndi wodetsedwa sadzabweranso mwa iwe.+
2 Iwe Yerusalemu dzuka, sansa fumbi ndipo ukhale pampando.
Masula zingwe zimene zili mʼkhosi mwako, iwe mwana wamkazi wa Ziyoni* amene unagwidwa nʼkutengedwa kupita kudziko lina.+
3 Chifukwa Yehova wanena kuti:
4 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti:
“Poyamba anthu anga anapita kukakhala ku Iguputo ngati alendo.+
Kenako Asuri anawapondereza popanda chifukwa.
5 Tsopano kodi nditani pamenepa?” akutero Yehova.
“Chifukwa anthu anga anatengedwa kwaulere.
Amene ankawalamulira ankangokhalira kufuula posonyeza kuti apambana.+
Tsiku lililonse ndinkaona kuti dzina langa silikulemekezedwa,”+ akutero Yehova.
6 “Pa chifukwa chimenecho anthu anga adzadziwa dzina langa.+
Pa chifukwa chimenecho adzadziwa pa tsiku limenelo kuti ineyo ndi amene ndikulankhula.
Ndithu ndi ineyo.”
7 Mapazi a munthu amene akuyenda pamwamba pa mapiri pobweretsa uthenga wabwino ndi okongola kwambiri!+
Munthu amene akulengeza za mtendere,+
Amene akubweretsa uthenga wabwino wa zinthu zabwino,
Amene akulengeza za chipulumutso,
Amene akuuza Ziyoni kuti: “Mulungu wako wakhala Mfumu.”+
8 Tamvera! Alonda ako akufuula.
Onse akufuula pamodzi mosangalala,
Chifukwa akuona bwinobwino pamene Yehova akusonkhanitsanso anthu okhala mu Ziyoni.
9 Inu mabwinja a mu Yerusalemu+ sangalalani, nonse pamodzi mufuule mosangalala,
Chifukwa Yehova watonthoza anthu ake+ ndipo wawombola Yerusalemu.+
10 Yehova waika poyera dzanja lake loyera kuti mitundu yonse ione.+
Ndipo malekezero onse a dziko lapansi adzaona zimene Mulungu wathu wachita potipulumutsa.*+
11 Chokanimo, chokanimo, tulukani mmenemo,+ musakhudze chinthu chilichonse chodetsedwa!+
12 Chifukwa simudzachoka mopanikizika,
Ndipo simudzafunika kuthawa,
Popeza Yehova azidzayenda patsogolo panu,+
Ndipo Mulungu wa Isiraeli azidzalondera kumbuyo kwanu.+
13 Taona! Mtumiki wanga+ azidzachita zinthu mwanzeru.
Adzapatsidwa udindo wapamwamba
Adzakwezedwa ndipo adzalemekezedwa kwambiri.+
14 Panali anthu ambiri amene ankamuyangʼana modabwa,
Chifukwa maonekedwe ake anali atasintha kwambiri kuposa a munthu wina aliyense,
Ndipo kukongola kwa thupi lake kunali kutatha, sanalinso wokongola kuposa anthu,
15 Mofanana ndi zimenezi iye adzadabwitsa mitundu yambiri ya anthu.+
Mafumu akadzamuona adzatseka pakamwa pawo,*+
Chifukwa iwo adzaona zimene sanauzidwepo,
Ndipo adzaganizira zimene sanamvepo.+
53 Kodi ndi ndani amene wakhulupirira zinthu zimene anamva kwa ife?*+
Ndipo kodi dzanja la Yehova+ laonetsedwa kwa ndani?+
2 Iye adzaphuka ngati nthambi+ pamaso pawinawake* ndiponso ngati muzu wotuluka mʼnthaka youma.
Saoneka ngati munthu wapadera kapena waulemerero,+
Ndipo tikamuona, maonekedwe ake si ochititsa chidwi moti ife nʼkukopeka naye.*
3 Iye ananyozedwa ndipo anthu ankamupewa,+
Anali munthu amene kupweteka ankakudziwa bwino* ndipo matenda ankawadziwa.
Zinali ngati kuti nkhope yake yabisika kwa ife.*
Ananyozedwa ndipo tinkamuona ngati wopanda pake.+
Koma ifeyo tinkamuona ngati munthu amene wagwidwa ndi matenda, amene walangidwa* ndi Mulungu ndiponso kuzunzidwa.
Analandira chilango kuti ife tikhale pamtendere,+
Ndipo chifukwa cha mabala ake ifeyo tinachiritsidwa.+
6 Tonsefe tikungoyendayenda uku ndi uku ngati nkhosa zosochera.+
Aliyense akulowera njira yake
Ndipo Yehova wachititsa kuti zolakwa za tonsefe zigwere pa ameneyo.+
Anamutengera kumalo oti akamuphere ngati nkhosa,+
Mofanana ndi nkhosa yaikazi imene yangokhala chete pamene akufuna kuimeta ubweya,
Ndipo sanatsegule pakamwa pake.+
8 Iye anaponderezedwa ndipo anatengedwa popanda kuweruzidwa mwachilungamo.
Ndi ndani amene anaganizira tsatanetsatane wa mʼbadwo wa makolo ake?*
Popeza iye anadulidwa mʼdziko la anthu amoyo.+
9 Anapatsidwa manda* limodzi ndi anthu oipa,+
Ndipo pamene anafa anaikidwa mʼmanda limodzi ndi anthu olemera,*+
Ngakhale kuti iye sanalakwe chilichonse*
Ndipo mʼkamwa mwake munalibe chinyengo.+
10 Koma Yehova ndi amene anafuna* kuti mtumiki wake aphwanyidwe ndipo anamulola kuti adwale.
Ngati mungapereke moyo wake kuti ukhale nsembe yakupalamula,+
Iye adzaona ana ake,* adzakhala ndi moyo kwa nthawi yaitali,+
11 Chifukwa cha kuvutika kwake, iye adzaona zabwino ndipo adzakhutira.
Chifukwa cha zimene mtumiki wanga wolungama akudziwa,+
Adzachititsa kuti anthu ambiri azionedwa olungama,+
Ndipo adzanyamula zolakwa zawo.+
12 Pa chifukwa chimenechi, ndidzamupatsa gawo pamodzi ndi ambiri,
Ndipo iye adzagawana ndi amphamvu katundu amene alanda kunkhondo,
Chifukwa anapereka moyo wake*+
Ndipo anaikidwa mʼgulu la anthu ochimwa.+
Ananyamula tchimo la anthu ambiri+
Ndipo analowererapo kuti athandize anthu ochimwa.+
54 “Fuula mosangalala iwe mkazi amene sunaberekepo mwana.+
Iwe amene sunamvepo zowawa za pobereka,+ sangalala ndipo ufuule mosangalala.+
Chifukwa ana a mkazi wosiyidwa ndi ambiri
Kuposa ana a mkazi yemwe ali ndi mwamuna,”*+ akutero Yehova.
Tambasula nsalu za chihema chako chachikulu.
Usaumire pochita zimenezi. Talikitsa zingwe za tenti yako
Ndipo ulimbitse zikhomo zake.+
3 Chifukwa mudzafalikira mbali yakumanja ndi kumanzere.
Ana ako adzatenga mitundu ya anthu kukhala yawo,
Ndipo adzakhala mʼmizinda imene inasiyidwa yabwinja.+
4 Usachite mantha,+ chifukwa sudzachititsidwa manyazi.+
Usachite manyazi, chifukwa sudzakhumudwitsidwa.
Iwe udzaiwala manyazi apaubwana wako,
Ndipo sudzakumbukiranso kunyozeka kwa paumasiye wako.
5 Chifukwa Wokupanga Wamkulu+ ali ngati mwamuna* wako,+
Dzina lake ndi Yehova wa magulu ankhondo akumwamba,
Ndipo Woyera wa Isiraeli ndiye Wokuwombola.+
Iye adzatchedwa Mulungu wa dziko lonse lapansi.+
6 Yehova anakuitana ngati kuti unali mkazi wosiyidwa komanso amene ali ndi chisoni,*+
Ngati mkazi amene anakwatiwa ali mtsikana kenako nʼkusiyidwa,” akutero Mulungu wako.
8 Chifukwa cha mkwiyo wanga waukulu ndinakubisira nkhope yanga kwa kanthawi,+
Koma chifukwa cha chikondi changa chokhulupirika chimene sichidzatha ndidzakuchitira chifundo,”+ akutero Yehova, Wokuwombola.+
9 “Kwa ine, zimenezi zili ngati masiku a Nowa.+
Monga mmene ndinalumbirira kuti madzi amʼnthawi ya Nowa sadzamizanso dziko lapansi,+
Ndikulumbiranso kuti sindidzakukwiyira kapena kukudzudzula.+
10 Mapiri akhoza kuchotsedwa,
Ndipo zitunda zikhoza kugwedezeka,
Koma chikondi changa chokhulupirika sichidzachotsedwa pa iwe,+
Ndipo pangano langa lamtendere silidzagwedezeka,”+ akutero Yehova, amene akukuchitira chifundo.+
11 “Iwe mkazi amene uli pamavuto,+ amene ukukankhidwa ndi mphepo yamkuntho ndiponso amene sunatonthozedwe,+
Ine ndikukumanga ndi miyala komanso simenti yolimba,
Ndipo ndikumanga maziko ako ndi miyala ya safiro.+
12 Nsanja za mpanda wa mzinda wako ndidzazimanga ndi miyala ya rube,
Mageti ako ndidzawamanga ndi miyala yonyezimira,*
Ndipo mpanda wonse wa mzinda wako ndidzaumanga ndi miyala yamtengo wapatali.
14 Udzakhazikika molimba mʼchilungamo.+
Palibe amene adzakupondereze,+
Sudzaopa kanthu ndipo palibe chimene chidzakuchititse mantha,
Chifukwa palibe chilichonse choopsa chimene chidzakuyandikire.+
15 Ngati aliyense atakuukira,
Sadzakhala kuti watumidwa ndi ine.
Aliyense amene adzakuukire adzagwa chifukwa cha iwe.+
16 Ine ndi amene ndinalenga mmisiri,
Amene amauzira moto wamakala
Nʼkupanga chida chankhondo ndi luso lake.
Ine ndinalenganso munthu wowononga kuti aziwononga.+
17 Chida chilichonse chimene chidzapangidwe kuti chikuvulaze sichidzapambana,+
Ndipo lilime lililonse limene lidzalimbane nawe pamlandu udzalitsutsa.
Ichi ndi cholowa cha atumiki a Yehova,
Ndipo chilungamo chawo nʼchochokera kwa ine,” akutero Yehova.+
55 Inu nonse amene mukumva ludzu,+ bwerani mudzamwe madzi.+
Inu amene mulibe ndalama, bwerani mudzagule kuti mudye.
Inde bwerani mudzagule vinyo ndi mkaka+ popanda ndalama ndiponso popanda mtengo.+
2 Nʼchifukwa chiyani anthu inu mukuwononga ndalama polipirira zinthu zimene si chakudya,
Ndipo nʼchifukwa chiyani mukuwononga ndalama* zimene mwapeza polipirira zinthu zimene nʼzosakhutitsa?
3 Tcherani khutu lanu ndipo mubwere kwa ine.+
Mverani ndipo mudzapitiriza kukhala ndi moyo,
Ndithu ine ndidzachita nanu pangano limene lidzakhalepo mpaka kalekale+
Lokhudza chikondi chokhulupirika chimene ndinalonjeza Davide. Lonjezo limeneli ndi lodalirika.+
4 Taonani! Ine ndinamuchititsa kuti akhale mboni+ ku mitundu ya anthu,
Ndiponso kuti akhale mtsogoleri+ ndi wolamulira+ wa mitundu ya anthu.
5 Iwe udzaitana mtundu umene sukuudziwa,
Ndipo anthu a mtundu umene sukukudziwa adzathamangira kwa iwe
Chifukwa cha Yehova Mulungu wako,+ Woyera wa Isiraeli,
Komanso chifukwa chakuti adzakupatsa ulemerero.+
6 Funafunani Yehova pa nthawi imene akupezeka.+
Muitaneni adakali pafupi.+
7 Munthu woipa asiye njira yake+
Ndipo wopweteka anzake asiye maganizo ake.
Iye abwerere kwa Yehova ndipo adzamuchitira chifundo.+
Abwerere kwa Mulungu wathu, chifukwa adzamukhululukira ndi mtima wonse.+
8 “Maganizo anga ndi osiyana ndi maganizo anu,+
Ndipo njira zanu ndi zosiyana ndi njira zanga,” akutero Yehova.
9 “Chifukwa mofanana ndi kumwamba kumene kuli pamwamba kuposa dziko lapansi,
Njira zanganso nʼzapamwamba kuposa njira zanu
Ndipo maganizo anga ndi apamwamba kuposa maganizo anu.+
10 Mofanana ndi mvula komanso sinowo* zimene zimagwa kuchokera kumwamba
Ndipo sizibwerera kumeneko mpaka zitanyowetsa kwambiri nthaka nʼkuchititsa kuti mbewu zimere ndi kubereka zipatso,
Nʼkupereka mbewu kuti anthu adzale komanso chakudya kuti adye,
Sadzabwerera kwa ine popanda kukwaniritsa cholinga chake,+
Koma adzachitadi chilichonse chimene ine ndikufuna,+
Ndipo zimene ndinawatumizira kuti achite zidzachitikadi.
Mukadzafika, mapiri ndi zitunda zidzafuula mosangalala,+
Ndipo mitengo yonse yakutchire idzawomba mʼmanja.+
13 Mʼmalo mwa chitsamba chaminga padzamera mtengo wa junipa.*+
Mʼmalo mwa chomera choyabwa padzamera mtengo wa mchisu.
Zinthu zimenezi zidzachititsa kuti Yehova atchuke,*+
Ndipo zidzakhala chizindikiro chamuyaya chimene sichidzawonongeka.”
56 Yehova wanena kuti:
“Tsatirani chilungamo+ ndipo chitani zolungama,
Chifukwa chipulumutso changa chatsala pangʼono kubwera
Ndipo chilungamo changa chidzaonekera.+
2 Wosangalala ndi munthu amene amachita zimenezi,
Ndiponso mwana wa munthu amene amatsatira zimenezi,
Amene amasunga Sabata ndipo salidetsa+
Komanso amaletsa dzanja lake kuti lisachite choipa chilichonse.
3 Mlendo amene wayamba kulambira Yehova+ asanene kuti,
‘Ndithu Yehova adzandilekanitsa ndi anthu ake.’
Ndipo munthu wofulidwa asanene kuti, ‘Inetu ndine mtengo wouma.’”
4 Izi nʼzimene Yehova wanena kwa anthu ofulidwa amene amasunga sabata langa. Amene asankha kuchita zimene ndimasangalala nazo komanso amene amatsatira pangano langa:
5 “Mʼnyumba mwanga ndiponso mkati mwa mpanda wanga ndidzawapatsa chipilala chachikumbutso ndiponso dzina,
Zomwe ndi zabwino kwambiri kuposa ana aamuna ndi aakazi.
Ndidzawapatsa dzina limene lidzakhalapo mpaka kalekale,
Dzina limene silidzatha.
6 Ndipo alendo amene abwera kwa Yehova kuti amutumikire,
Kuti azikonda dzina la Yehova+
Ndiponso kuti akhale atumiki ake,
Onse amene amasunga Sabata ndipo salidetsa
Komanso amene amatsatira pangano langa,
7 Nawonso ndidzawabweretsa kuphiri langa loyera+
Ndipo ndidzawachititsa kuti asangalale mʼnyumba yanga yopemphereramo.
Nsembe zawo zopsereza zathunthu ndi nsembe zawo zina ndidzazilandira paguwa langa lansembe.
Chifukwa nyumba yanga idzatchedwa nyumba yopemphereramo anthu a mitundu yonse.”+
8 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, amene akusonkhanitsa pamodzi Aisiraeli omwe anabalalitsidwa,+ wanena kuti:
“Ine ndidzamusonkhanitsira anthu ena kuwonjezera pa anthu ake amene anasonkhanitsidwa kale.”+
10 Alonda ake ndi akhungu+ ndipo palibe amene akudziwa zimene zichitike.+
Onsewo ndi agalu opanda mawu ndipo satha kuuwa.+
Amangokhalira kupuma wefuwefu ndi kugona pansi. Amakonda kugona tulo.
11 Iwo ndi agalu adyera kwambiri
Ndipo sakhuta.
Iwo ndi abusa osamvetsa zinthu.+
Onse apatukira kunjira yawo.
Aliyense wa iwo akufunafuna njira yopezera phindu lachinyengo ndipo akunena kuti:
Mawa lidzakhalanso ngati lero, mwinanso kuposa pamenepa.”
57 Wolungama wawonongedwa,
Koma palibe amene zikumukhudza.
2 Iye amalowa mumtendere.
Onse amene amayenda mowongoka amapita kukapuma mʼmanda.*
4 Kodi mukumuseka ndani?
Kodi mukuyasamulira ndani pakamwa panu ndi kumutulutsira lilime?
Kodi inu si ana a machimo,
Ana a chinyengo,+
5 Amene mukukhala ndi chilakolako champhamvu chogonana pakati pa mitengo ikuluikulu,+
Pansi pa mtengo uliwonse wa masamba ambiri?+
Kodi si inu amene mumapha ana mʼzigwa,*+
Pakati pa matanthwe?
6 Gawo lako lili pamodzi ndi miyala yosalala yamʼchigwa.*+
Inde, gawo lako ndi limeneli.
Ndipo umapereka nsembe zachakumwa, ndiponso mphatso kwa zinthu zimenezi.+
Kodi ine ndikhutire* ndi zinthu zimenezi?
7 Bedi lako unaliika pamwamba pa phiri lalitali ndi lokwezeka.+
Ndipo unapita kumeneko kukapereka nsembe.+
8 Unaika chizindikiro chachikumbutso chako kuseri kwa chitseko ndi kuseri kwa felemu.
Iwe unandisiya ndipo unavula.
Unakwera mtunda nʼkukulitsa bedi lako.
Ndipo unachita nawo pangano.
Unatumiza nthumwi zako kutali kwambiri,
Moti mpaka unatsikira mʼManda.*
10 Watopa chifukwa chotsatira njira zako zambiri,
Koma sunanene kuti, ‘Nʼzopanda phindu!’
Unapeza mphamvu zina.
Nʼchifukwa chake sunafooke.*
Ine sunandikumbukire.+
Palibe chimene unaganizira mumtima mwako.+
Kodi si paja ine ndinakhala chete ndipo sindinachitepo kanthu pa zochita zako?+
Choncho iweyo sunkandiopa.
Mphepo idzaulutsa mafano onsewo
Ndipo mpweya udzawakankhira kutali,
Koma munthu amene amathawira kwa ine adzalandira dziko
Ndipo adzatenga phiri langa loyera kukhala lake.+
14 Ndiyeno wina adzanena kuti, ‘Konzani msewu! Konzani msewu! Konzani njira!+
Chotsani chopinga chilichonse panjira ya anthu anga.’”
15 Chifukwa Wapamwamba ndi Wokwezeka,
Amene adzakhalepo mpaka kalekale+ ndiponso dzina lake ndi loyera,+ wanena kuti:
“Ine ndimakhala pamalo apamwamba komanso oyera,+
Koma ndimakhalanso ndi anthu opsinjika ndiponso amene ali ndi mtima wodzichepetsa,
Kuti nditsitsimutse mtima wa anthu onyozeka
Ndiponso kuti nditsitsimutse mtima wa anthu opsinjika.+
16 Chifukwa ine sindidzatsutsana nawo mpaka kalekale
Kapena kukhala wokwiya nthawi zonse.+
Popeza mzimu wa munthu ukhoza kufooka chifukwa cha ine,+
Ngakhale zinthu zopuma zimene ine ndinapanga.
17 Ine ndinakwiya chifukwa cha machimo amene ankachita pofuna kupeza phindu mwachinyengo,+
Choncho ndinamulanga, ndinabisa nkhope yanga ndipo ndinakwiya.
Koma iye anapitiriza kuyenda ngati wopanduka,+ ankangotsatira zofuna za mtima wake.
18 Ine ndaona njira zake,
Koma ndidzamuchiritsa+ nʼkumutsogolera,+
Ndipo ndidzayambiranso kumutonthoza,+ iyeyo ndi anthu ake amene akulira.”+
19 “Ndikulenga chipatso cha milomo.
Mtendere wosatha udzaperekedwa kwa amene ali kutali
Ndiponso kwa amene ali pafupi+ ndipo ndidzamʼchiritsa,” akutero Yehova.
20 “Koma anthu oipa ali ngati nyanja imene ikuchita mafunde, imene singathe kukhala bata,
Ndipo madzi ake akuvundula zomera zamʼnyanjamo ndiponso matope.
21 Oipa alibe mtendere,”+ akutero Mulungu wanga.
58 Iye anandiuza kuti: “Fuula mwamphamvu! Usabweze mawu.
Kweza mawu ako ngati lipenga.
Uza anthu anga za kupanduka kwawo.+
A nyumba ya Yakobo uwauze machimo awo.
2 Amandifunafuna tsiku lililonse,
Ndipo amasonyeza kuti akusangalala kudziwa njira zanga,
Ngati kuti unali mtundu umene unkachita zinthu zolungama
Ndiponso sunasiye chilungamo cha Mulungu wawo.+
Iwo akundipempha chiweruzo cholungama,
Ngati kuti akufunitsitsa kuyandikira kwa Mulungu.+ Akunena kuti:
3 ‘Nʼchifukwa chiyani simukuona pamene tikusala kudya?+
Ndipo nʼchifukwa chiyani simukuona tikamadzisautsa?’+
Chifukwa chakuti pa tsiku lanu losala kudya mumachita zofuna zanu,*
Ndipo mumapondereza antchito anu.+
4 Mukamasala kudya zotsatira zake zimakhala kukangana komanso ndewu,
Ndipo mumamenya anzanu mwankhanza ndi zibakera.*
Simungamasale kudya ngati mmene mukuchitira panopa nʼkumayembekezera kuti mawu anu amveka kumwamba.
5 Kodi kusala kudya kumene ine ndinakulamulani nʼkumeneku?
Kodi likhale tsiku loti munthu azidzisautsa,
Kuti aziweramitsa mutu wake ngati udzu,
Ndiponso kuti aziyala chiguduli pabedi lake nʼkuwazapo phulusa?
Kodi kumeneku nʼkumene mumati kusala kudya komanso tsiku losangalatsa kwa Yehova?
6 Ayi, kusala kudya kumene ine ndimafuna ndi uku:
Kuti muchotse maunyolo amene munaika chifukwa cha kuipa mtima kwanu,
Kuti mumasule zingwe za goli,+
Kuti mumasule anthu oponderezedwa,+
Ndiponso kuti goli lililonse mulithyole pakati.
7 Ndimafunanso kuti muzigawira chakudya chanu anthu anjala,+
Kuti muziitanira mʼnyumba zanu anthu osauka ndi osowa pokhala,
Kuti mukaona munthu wamaliseche muzimuveka+
Ndiponso kuti musamadzibise kwa abale anu.
Chilungamo chanu chizidzayenda patsogolo panu,
Ndipo ulemerero wa Yehova uzidzalondera kumbuyo kwanu.+
9 Pa nthawiyo mudzaitana ndipo Yehova adzayankha.
Mudzafuula popempha thandizo ndipo iye adzanena kuti, ‘Ndikumva lankhulani!’
Mukachotsa goli pakati panu,
Nʼkusiya kulozana zala ndi kulankhulana zopweteka,+
10 Mukapatsa munthu wanjala zinthu zimene inuyo mukulakalaka,*+
Ndiponso mukapereka zinthu zofunika kwa anthu ovutika,
Kuunika kwanu kudzawala ngakhale mumdima,
Ndipo mdima wanu waukulu udzakhala ngati masana.+
11 Yehova azidzakutsogolerani nthawi zonse
Ndipo adzakupatsani zinthu zofunika ngakhale mʼdziko louma.+
Iye adzalimbitsa mafupa anu
Ndipo inu mudzakhala ngati dimba lothiriridwa bwino,+
Ndiponso ngati kasupe amene madzi ake saphwera.
12 Chifukwa cha inu, anthu adzamanganso mabwinja akalekale,+
Ndipo mudzabwezeretsa maziko a mibadwo yakale.+
Mudzatchedwa womanga makoma ogumuka,+
Ndiponso wokonza misewu kuti anthu azikhala mʼmphepete mwake.
13 Ngati chifukwa cha Sabata mukupewa* kuchita zofuna zanu* pa tsiku langa lopatulika,+
Ndipo mukanena kuti Sabata ndi tsiku losangalatsa kwambiri, tsiku lopatulika la Yehova, tsiku loyenera kulemekezedwa,+
Ndipo mukalilemekeza mʼmalo mochita zofuna zanu ndiponso mʼmalo molankhula zopanda pake,
14 Mukatero mudzasangalala kwambiri mwa Yehova,
Ndipo ine ndidzakuchititsani kuti mukwere mʼmalo apamwamba a dziko lapansi.+
Ndidzakuchititsani kuti mudye* zochokera mʼcholowa cha Yakobo kholo lanu,+
Chifukwa pakamwa pa Yehova panena.”
2 Ayi si choncho. Koma zolakwa zanu nʼzimene zakulekanitsani ndi Mulungu wanu.+
Machimo anu ndi amene amuchititsa kuti akubisireni nkhope yake,
Ndipo sakufuna kumva zimene mukunena.+
Milomo yanu imalankhula zabodza+ ndipo lilime lanu limanena zinthu zopanda chilungamo.
4 Palibe amene amafuula poikira kumbuyo chilungamo,+
Ndipo palibe amene amalankhula zoona akapita kukhoti.
Iwo amakhulupirira zinthu zachabechabe+ ndipo amalankhula zopanda pake.
Iwo atenga pakati pa mavuto ndipo abereka zopweteka.+
Aliyense amene angadye mazira awowo adzafa,
Ndipo mʼdzira limene lasweka mumatuluka mphiri.
Ntchito zawo nʼzopweteka ena,
Ndipo mʼmanja mwawo muli ntchito zachiwawa.+
Maganizo awo ndi maganizo oipa.
Zonse zimene amachita zimakhala zowononga ndiponso zobweretsa mavuto.+
Misewu yawo aikhotetsakhotetsa.
Palibe munthu aliyense woyenda mmenemo amene adzadziwe mtendere.+
9 Nʼchifukwa chake chilungamo chatitalikira kwambiri,
Ndipo zinthu zolungama sizikutipeza.
Tikuyembekezera kuwala, koma mʼmalomwake tikungoona mdima.
Tikuyembekezera tsiku lowala, koma tikupitirizabe kuyenda mumdima waukulu.+
10 Tikungopapasa khoma ngati anthu amene ali ndi vuto losaona,
Tikungopapasapapasa ngati anthu opanda maso.+
Tikupunthwa masanasana ngati kuti tili mumdima wamadzulo.
Pakati pa anthu amphamvu tikungokhala ngati anthu akufa.
11 Tonsefe tikungolira ngati zimbalangondo
Ndipo tikungokhalira kubuula momvetsa chisoni ngati njiwa.
Tikuyembekezera chilungamo koma sichikupezeka.
Tikuyembekezera chipulumutso koma chili kutali ndi ife.
12 Chifukwa zolakwa zathu zachuluka pamaso panu,+
Tchimo lathu lililonse likupereka umboni wotsutsana nafe.+
Zolakwa zathu zili pa ife,
Ndipo zochimwa zathu tikuzidziwa bwino.+
13 Ife tachimwa ndipo tamukana Yehova.
Tabwerera mʼmbuyo nʼkumusiya Mulungu wathu.
Tanena zinthu zopondereza ena komanso zopanduka.+
Taganizira mabodza oti tinene ndipo talankhula mawu achinyengo mumtima mwathu.+
14 Chilungamo chabwezedwa mʼmbuyo,+
Ndipo chilungamocho chaima patali.+
Chifukwa choonadi chapunthwa* mʼbwalo lamumzinda,
Ndipo zinthu zolungama zikulephera kulowamo.
16 Iye ataona kuti panalibe munthu aliyense woti nʼkuthandizapo,
Anadabwa kwambiri kuti palibe amene akulowererapo.
Choncho anapulumutsa anthu* ndi dzanja lake,
Ndipo chilungamo chake nʼchimene chinamulimbikitsa kuchita zimenezo.
17 Choncho iye anavala chilungamo ngati chovala chamamba achitsulo,
Anavala chilungamo ngati chovala kuti apereke chilango kwa adani ake+
Ndipo kuchita zinthu modzipereka kwambiri kunali ngati chovala chake chodula manja.
18 Iye adzawapatsa mphoto chifukwa cha zimene achita:+
Adani ake adzawapatsa mkwiyo ndipo anthu otsutsana naye adzawapatsa chilango.+
Ndipo zilumba adzazipatsa chilango chogwirizana ndi zochita zawo.
19 Amene ali kolowera dzuwa adzaopa dzina la Yehova,
Ndipo amene ali kotulukira dzuwa adzaopa ulemerero wake,
Chifukwa iye adzabwera ngati mtsinje wothamanga,
Umene ukuyendetsedwa ndi mzimu wa Yehova.
20 “Wowombola+ adzabwera+ ku Ziyoni,
Adzabwera kwa mbadwa za Yakobo zimene zasiya zolakwa zawo,”+ akutero Yehova.
21 Yehova wanena kuti: “Koma pangano langa ndi iwowo ndi ili,+ mzimu wanga umene uli pa iwe ndi mawu anga amene ndaika mʼkamwa mwako, sizidzachotsedwa mʼkamwa mwako, mʼkamwa mwa ana ako* kapena mʼkamwa mwa zidzukulu zako,* kuyambira panopa mpaka kalekale,” akutero Yehova.
60 “Imirira mkazi iwe!+ Onetsa kuwala kwako, chifukwa kuwala kwako kwafika.
Ulemerero wa Yehova wakuunikira.+
2 Taona! Mdima udzaphimba dziko lapansi,
Ndipo mdima wandiweyani udzaphimba mitundu ya anthu.
Koma kuwala kwa Yehova kudzafika pa iwe,
Ndipo ulemerero wake udzaonekera pa iwe.
4 Kweza maso ako uone zonse zimene zikuchitika mokuzungulira.
Onse asonkhanitsidwa pamodzi. Akubwera kwa iwe.
5 Pa nthawi imeneyo, udzaona zimenezi ndipo nkhope yako idzasangalala.+
Mtima wako udzagunda mwamphamvu ndipo udzasangalala kwambiri,
Chifukwa chuma chamʼnyanja adzachibweretsa kwa iwe.
Katundu wa mitundu ya anthu adzabwera kwa iwe.+
Anthu onse a ku Sheba adzabwera.
Adzabwera atanyamula golide ndi lubani.
Iwo adzatamanda Yehova pamaso pa anthu onse.+
7 Nkhosa zonse za ku Kedara+ zidzasonkhanitsidwa kwa iwe.
Nkhosa zamphongo za ku Nebayoti+ zidzakutumikira.
8 Kodi amene akubwera akuuluka ngati mtambowa ndi ndani?
Ndi ndani amene akubwera ngati nkhunda zimene zikuulukira mʼmakola awo?*
9 Chifukwa zilumba zidzayembekezera ine.+
Sitima zapamadzi za ku Tarisi zidzayembekezera ine ngati poyamba paja,
Kuti zikubweretsere ana ako aamuna kuchokera kutali,+
Atatenga siliva ndi golide wawo,
Kuti alemekeze dzina la Yehova Mulungu wako ndi Woyera wa Isiraeli,
10 Alendo adzamanga mipanda yako,
Ndipo mafumu awo adzakutumikira.+
Ine ndinakulanga chifukwa ndinali nditakwiya,
Koma chifukwa cha kukoma mtima kwanga* ndidzakuchitira chifundo.+
11 Mageti ako adzakhala otsegula nthawi zonse.+
Sadzatsekedwa masana kapena usiku
Kuti azikubweretsera chuma cha mitundu ya anthu,
Ndipo mafumu awo ndi amene adzakhale patsogolo pochita zimenezi.+
12 Chifukwa mtundu uliwonse ndi ufumu uliwonse umene sudzakutumikira udzawonongedwa,
Ndipo mitundu ya anthu idzasakazidwa kotheratu.+
13 Ulemerero wa Lebanoni udzabwera kwa iwe.+
Mtengo wa junipa,* mtengo wa ashi* ndiponso mtengo wa mkungudza zidzabwera pa nthawi imodzi,+
Kuti zikongoletse malo anga opatulika,
Ndipo ine ndidzalemekeza malo oikapo mapazi anga.+
14 Ana a anthu amene ankakupondereza adzabwera nʼkudzagwada pamaso pako.
Anthu onse amene ankakuchitira zachipongwe adzagwada pamapazi ako,
Ndipo adzakutchula kuti mzinda wa Yehova,
Ziyoni wa Woyera wa Isiraeli.+
15 Ngakhale kuti ndinakusiya komanso anthu ankadana nawe ndipo palibe aliyense ankadutsa mwa iwe,+
Ine ndidzachititsa kuti ukhale chinthu chimene anthu adzachitamanda mpaka kalekale,
Ndiponso chinthu chosangalatsa ku mibadwo yonse.+
16 Iwe udzamwa mkaka wa mitundu ya anthu,+
Ndipo udzayamwa bere la mafumu.+
Udzadziwadi kuti ine Yehova ndine Mpulumutsi wako,
Ndiponso kuti Wamphamvu wa Yakobo ndi Wokuwombola.+
17 Mʼmalo mwa kopa* ndidzabweretsa golide,
Mʼmalo mwa chitsulo ndidzabweretsa siliva,
Mʼmalo mwa mtengo ndidzabweretsa kopa,
Ndipo mʼmalo mwa miyala ndidzabweretsa chitsulo.
Ndidzaika mtendere kuti ukhale ngati okuyangʼanira,
Komanso chilungamo kuti chikhale ngati okupatsa ntchito.+
Mipanda yako udzaitcha Chipulumutso+ ndipo mageti ako udzawatcha Tamanda.
19 Dzuwa silidzakhalanso lokuunikira masana,
Ndipo mwezi sudzakuunikiranso.
Chifukwa Yehova adzakhala kuwala kwako mpaka kalekale,+
Ndipo Mulungu wako adzakhala kukongola kwako.+
20 Dzuwa lako silidzalowanso,
Ndipo mwezi wako sudzasiya kuwala,
Chifukwa Yehova adzakhala kuwala kwako mpaka kalekale,+
Ndipo masiku ako olira adzakhala atatha.+
21 Anthu ako onse adzakhala olungama.
Adzatenga dzikoli kukhala lawo mpaka kalekale.
22 Wamngʼono adzasanduka anthu 1,000,
Ndipo wochepa adzasanduka mtundu wamphamvu.
Ineyo Yehova ndidzapangitsa kuti zimenezi zichitike mofulumira pa nthawi yake.”
61 Mzimu wa Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, uli pa ine,+
Chifukwa Yehova anandidzoza kuti ndilengeze uthenga wabwino kwa anthu ofatsa.+
Anandituma kuti ndikamange mabala a anthu osweka mtima,
Kuti ndilengeze za ufulu kwa anthu amene anagwidwa nʼkutengedwa kupita kudziko lina,
Komanso kuti maso a akaidi adzatsegulidwa.+
2 Wandituma kuti ndilengeze za chaka cha Yehova chokomera anthu mtima,*
Ndi za tsiku lobwezera la Mulungu wathu,+
Komanso kuti nditonthoze anthu onse amene akulira,+
3 Kuti ndisamalire anthu onse amene akulirira Ziyoni,
Kuti ndiwapatse nsalu yovala kumutu mʼmalo mwa phulusa,
Kuti ndiwapatse mafuta kuti azisangalala mʼmalo molira,
Kuti ndiwapatse chovala choti azivala ponditamanda mʼmalo mokhala otaya mtima.
Ndipo iwo adzatchedwa mitengo ikuluikulu ya chilungamo,
4 Iwo adzamanganso malo amene akhala bwinja kwa nthawi yaitali.
Adzamanga malo amene anasakazidwa kalekale,+
Adzakonzanso mizinda imene inawonongedwa,+
Malo amene akhala ali osakazidwa kumibadwomibadwo.+
5 “Alendo adzabwera nʼkumaweta ziweto zanu,
Ndipo anthu ochokera kwina+ adzakhala olima minda yanu ndi osamalira minda yanu ya mpesa.+
Mudzadya zinthu zochokera kumitundu ya anthu+
Ndiponso mudzadzitamandira chifukwa cha ulemerero umene* mudzapeze kuchokera kwa iwo.
7 Mʼmalo mwa manyazi, mudzalandira madalitso ochuluka kuwirikiza kawiri,
Ndipo mʼmalo mochita manyazi, mudzafuula mosangalala chifukwa cha gawo lanu.
Inde, mudzalandira madalitso owirikiza kawiri mʼdziko lanu,+
Ndipo mudzasangalala mpaka kalekale.+
8 Chifukwa ine Yehova ndimakonda chilungamo.+
Ndimadana ndi zauchifwamba komanso zinthu zopanda chilungamo.+
Anthu anga ndidzawapatsa malipiro awo mokhulupirika,
Ndipo ndidzachita nawo pangano lomwe lidzakhalapo mpaka kalekale.+
9 Ana awo* adzadziwika pakati pa mitundu ya anthu,+
Ndipo mbadwa zawo zidzadziwika pakati pa anthu osiyanasiyana.
10 Ndidzasangalala kwambiri mwa Yehova.
Ndidzasangalala mwa Mulungu wanga ndi mtima wanga wonse.+
Chifukwa iye wandiveka zovala zachipulumutso.+
Wandiveka mkanjo wa chilungamo,*
Ngati mkwati amene wavala nduwira yofanana ndi ya wansembe,+
Ndiponso ngati mkwatibwi amene wavala zinthu zake zodzikongoletsera.
11 Chifukwa mofanana ndi dziko lapansi limene limatulutsa zomera zake,
Ndiponso mofanana ndi munda umene umameretsa zinthu zimene zadzalidwa mmenemo,
Nayenso Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa,
Adzachititsa kuti chilungamo+ komanso mawu otamanda zimere+ pamaso pa mitundu yonse.
62 Chifukwa cha Ziyoni sindidzakhala chete,+
Ndipo chifukwa cha Yerusalemu sindidzakhala phee
Mpaka kulungama kwake kutawala kwambiri,+
Ndiponso mpaka chipulumutso chake chitakhala ngati muuni woyaka moto.+
3 Udzakhala chisoti chokongola mʼdzanja la Yehova,
Ndiponso nduwira yachifumu mʼdzanja la Mulungu wako.
Koma dzina lako lidzakhala Ndimakondwera Naye,+
Ndipo dziko lako lidzatchedwa Mkazi Wokwatiwa.
Chifukwa Yehova adzasangalala nawe,
Ndipo dziko lako lidzakhala ngati mkazi wokwatiwa.
5 Chifukwa mofanana ndi mmene mnyamata amakwatirira namwali,
Ana ako aamuna adzakukwatira.
Ngati mmene mkwati amasangalalira chifukwa cha mkwatibwi,
Mulungu wako adzasangalala chifukwa cha iwe.+
6 Iwe Yerusalemu, ine ndaika alonda pamakoma a mpanda wako.
Nthawi zonse, masana onse komanso usiku wonse, iwo asakhale chete.
Inu amene mukutchula dzina la Yehova,
Musapumule,
7 Ndipo pitirizani kupemphera kwa iye mpaka atakhazikitsa Yerusalemu,
Inde, mpaka atamusandutsa chinthu choti anthu padziko lonse azichitamanda.”+
8 Yehova walumbira atakweza dzanja lake lamanja ndiponso mkono wake wamphamvu kuti:
“Sindidzaperekanso mbewu zanu kwa adani anu kuti chikhale chakudya chawo,
Ndipo alendo sadzamwa vinyo wanu watsopano amene munamupeza movutikira.+
9 Koma anthu amene adzakolole mbewuzo ndi amene adzazidye ndipo adzatamanda Yehova.
Amene adzakolole mphesa ndi amene adzamwe vinyoyo mʼmabwalo anga oyera.”+
10 Dutsani mʼmageti, dutsani mʼmageti.
Lambulani njira kuti anthu adutse.+
Konzani msewu, konzani msewu waukulu.
Muchotsemo miyala.+
Anthu a mitundu yosiyanasiyana muwakwezere chizindikiro+
11 Taonani! Yehova walengeza mpaka kumalekezero a dziko lapansi kuti:
Taona! Mphoto yake ili ndi iyeyo,
Ndipo malipiro amene amapereka ali pamaso pake.’”+
12 Iwo adzatchedwa anthu oyera, anthu amene Yehova anawawombola,+
Ndipo iwe udzatchedwa Mzinda Umene Mulungu Anaufunafuna, Mzinda Umene Sanausiyiretu.+
63 Kodi amene akuchokera ku Edomuyu+ ndi ndani,
Amene akuchokera ku Bozira+ atavala zovala zowala zamitundu yosiyanasiyana,*
Amene zovala zake ndi zaulemelero,
Ndiponso amene akuyenda ndi mphamvu zake zochuluka?
“Ndine, amene ndikulankhula mwachilungamo,
Amene ndili ndi mphamvu zambiri zotha kupulumutsa.”
2 Nʼchifukwa chiyani zovala zanu zili zofiira,
Ndipo nʼchifukwa chiyani zovala zanu zikuoneka ngati za munthu woponda mphesa mʼchoponderamo mphesa?+
3 “Moponderamo mphesa ndapondapondamo ndekha.
Palibe munthu wochokera pakati pa mitundu ya anthu amene anali nane.
Ndinapitiriza kupondaponda adani anga nditakwiya,
Ndipo ndinkawapondaponda ndili ndi ukali.+
Magazi awo anawazikira pazovala zanga,
Ndipo ndadetsa zovala zanga zonse.
5 Ndinayangʼana koma panalibe wondithandiza.
Ndinadabwa kuti palibe amene anandithandiza.
6 Ndinapondaponda mitundu ya anthu nditakwiya,
Ndinawaledzeretsa ndi ukali wanga.+
Ndipo magazi awo ndinawathira pansi.”
7 Ndidzanena za ntchito za Yehova zosonyeza chikondi chake chokhulupirika,
Ntchito zotamandika za Yehova,
Chifukwa cha zinthu zonse zimene Yehova watichitira.+
Zinthu zabwino zambiri zimene wachitira nyumba ya Isiraeli,
Mogwirizana ndi chifundo chake komanso chikondi chake chokhulupirika chomwe ndi chochuluka.
8 Iye anati: “Ndithu awa ndi anthu anga, ana amene sadzachita zosakhulupirika.”*+
Choncho iye anakhala Mpulumutsi wawo.+
9 Pa nthawi yonse imene iwo ankavutika, iye ankavutikanso.+
Ndipo mthenga wake* anawapulumutsa.+
Iye anawawombola chifukwa cha chikondi komanso chifundo chake,+
Ndipo nthawi zonse ankawakweza mʼmwamba komanso kuwanyamula.+
10 Koma iwo anapanduka+ nʼkumvetsa chisoni mzimu wake woyera.+
11 Iwo anakumbukira masiku akale,
Masiku a Mose mtumiki wake,
Ndipo anafunsa kuti: “Kodi amene anawatulutsa mʼnyanja+ pamodzi ndi abusa a anthu ake+ uja ali kuti?
Ali kuti amene anaika mzimu wake woyera mwa iye?+
12 Ali kuti amene anachititsa mkono wake waulemerero kuti upite ndi dzanja lamanja la Mose,+
Amene anagawanitsa madzi pamaso pawo+
Kuti adzipangire dzina lomwe lidzakhalapo mpaka kalekale,+
13 Amene anawachititsa kuti adutse pamadzi amphamvu*
Moti anayenda osapunthwa,
Mofanana ndi hatchi mʼchipululu?*
15 Yangʼanani muli kumwamba ndipo muone
Kuchokera pamalo anu okhala apamwamba, oyera ndi aulemerero.*
Kodi mtima wanu wodzipereka kwambiri ndiponso mphamvu zanu zili kuti?
Kodi chikondi chanu chachikulu*+ ndi chifundo chanu+ zili kuti?
Chifukwa simukundisonyezanso zimenezi.
Ngakhale kuti Abulahamu sankatidziwa
Ndipo Isiraeli sangatizindikire,
Inu Yehova ndinu Atate wathu.
Dzina lanu ndinu Wotiwombola wakalekale.+
17 Nʼchifukwa chiyani inu Yehova mukuchititsa kuti tichoke panjira zanu?
Nʼchifukwa chiyani mukuumitsa mtima wathu kuti tisakuopeni?+
Bwererani chifukwa cha atumiki anu,
Mafuko omwe ndi cholowa chanu.+
18 Dzikoli linali la anthu anu oyera kwa kanthawi kochepa.
Koma adani athu apondaponda malo anu opatulika.+
19 Kwa nthawi yaitali, takhala ngati anthu amene simunawalamulirepo,
Ngati anthu amene sanadziwikepo ndi dzina lanu.
64 Zikanakhalatu bwino mukanangʼamba kumwamba nʼkutsika pansi pano,
Kuti mapiri agwedezeke chifukwa cha inu,
2 Ngati mmene zimakhalira moto ukayatsa tchire la zitsamba,
Ndiponso ukachititsa kuti madzi awire.
Zikanatero adani anu akanadziwa dzina lanu,
Ndipo mitundu ya anthu ikanachita mantha pamaso panu.
3 Pamene munachita zinthu zochititsa mantha zimene sitinkayembekezera,+
Munatsika ndipo mapiri anagwedezeka pamaso panu.+
4 Kuyambira kalekale palibe amene anamvapo, kuganizira,
Kapena kuona Mulungu wina kupatulapo inu,
Amene mumathandiza anthu omwe amayembekezera inu moleza mtima.+
5 Mwabwera kudzathandiza anthu amene amachita zinthu zolungama mosangalala,+
Anthu amene amakukumbukirani komanso kutsatira njira zanu.
Koma inu munakwiya chifukwa chakuti ifeyo tinkangopitiriza kuchimwa,+
Tinakhala tikuchimwa kwa nthawi yaitali.
Ndiye kodi panopa ndife oyenera kupulumutsidwa?
6 Tonse takhala ngati munthu wodetsedwa,
Ndipo zochita zathu zonse zolungama zili ngati kansalu kamene mkazi amavala pa nthawi yosamba.+
Tonsefe tidzanyala ngati tsamba,
Ndipo zolakwa zathu zidzatiuluzira kutali ngati mphepo.
7 Palibe amene akutchula dzina lanu popemphera,
Palibe amene akuyesetsa kuti mumuthandize,
Mwatibisira nkhope yanu,+
Ndipo mwatichititsa kuti tikumane ndi mavuto* chifukwa cha zolakwa zathu.
8 Koma inu Yehova, ndinu Bambo wathu.+
Chonde, kumbukirani kuti tonsefe ndi anthu anu.
10 Mizinda yanu yoyera yasanduka chipululu.
Ziyoni wasanduka chipululu,
Ndipo Yerusalemu wasanduka bwinja.+
11 Nyumba yathu yoyera* ndiponso yaulemerero,*
Imene makolo athu ankakutamandiranimo,
Yawotchedwa ndi moto,+
Ndipo zinthu zathu zonse zimene tinkaziona kuti ndi zamtengo wapatali zasanduka mabwinja
12 Poona zinthu zonsezi, kodi mupitiriza kumangokhala osachitapo kanthu, inu Yehova?
Kodi mungokhala chete nʼkumaonerera ife tikusautsidwa koopsa?+
65 “Ine ndalola kuti anthu amene sanafunse za ine andifunefune.
Ndalola kuti anthu amene sanandifunefune andipeze.+
Mtundu umene sunaitane pa dzina langa ndauuza kuti, ‘Ndili pano, ndili pano!’+
2 Ndatambasula manja anga tsiku lonse kwa anthu amakani,+
Kwa anthu amene akuyenda mʼnjira yoipa,+
Potsatira maganizo awo,+
3 Anthu amene amandikhumudwitsa nthawi zonse mopanda manyazi,+
Amene amapereka nsembe mʼminda+ komanso kufukiza nsembe zautsi panjerwa.
4 Iwo amakhala pansi kumanda,+
Ndipo usiku wonse amakhala mʼmalo obisika,*
Nʼkumadya nyama ya nkhumba,+
Ndipo mʼmiphika yawo muli msuzi wa zinthu zodetsedwa.+
Iwo ali ngati utsi mʼmphuno mwanga, ngati moto umene ukuyaka tsiku lonse.
6 Taonani! Zalembedwa pamaso panga.
Ine sindikhala chete,
Koma ndiwabwezera,+
Ndiwabwezera nʼkuwapatsa chilango chifukwa cha zonse zimene achita,*
7 Chifukwa cha zolakwa zawo komanso zolakwa za makolo awo,”+ akutero Yehova.
“Chifukwa choti afukiza nsembe zautsi pamapiri
Ndipo andinyoza pazitunda,+
Ine ndiwayezera malipiro awo onse choyamba.”*
8 Yehova wanena kuti:
“Munthu angathe kugwiritsa ntchito phava la mphesa popanga vinyo watsopano
Ndipo wina amanena kuti, ‘Musaliwononge, chifukwa muli zinthu zabwino* mmenemu.’
Inenso ndidzachita zofanana ndi zimenezi chifukwa cha atumiki anga,
Sindidzawawononga onse.+
9 Mwa Yakobo ndidzatulutsamo mwana*
Ndipo mwa Yuda ndidzatulutsamo amene adzalandire mapiri anga ngati cholowa chake.+
Anthu anga osankhidwa adzatenga dziko lamapiriro kuti likhale lawo,
Ndipo atumiki anga adzakhala mmenemo.+
10 Sharoni+ adzakhala malo odyetserako nkhosa
Ndipo chigwa cha Akori+ chidzakhala malo opumulirapo ngʼombe,
Anthu anga amene akundifunafuna ndidzawachitira zimenezi.
11 Koma inu muli mʼgulu la anthu amene asiya Yehova,+
Anthu amene aiwala phiri langa loyera,+
Amene amayalira tebulo mulungu wa Mwayi,
Komanso amene amadzaza makapu ndi vinyo wosakaniza nʼkupereka kwa mulungu wa Zokonzedweratu.
12 Choncho ine ndikonzeratu zoti inu mudzaphedwe ndi lupanga,+
Ndipo nonsenu mudzawerama kuti muphedwe,+
Chifukwa ine ndinakuitanani koma simunayankhe,
Ndinalankhula koma simunamvetsere.+
Munapitiriza kuchita zinthu zoipa pamaso panga
Ndipo munasankha zinthu zimene sizinandisangalatse.”+
13 Choncho Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti:
“Atumiki anga adzadya, koma inu mudzakhala ndi njala.+
Atumiki anga adzamwa,+ koma inu mudzakhala ndi ludzu.
Atumiki anga adzasangalala,+ koma inu mudzachita manyazi.+
14 Atumiki anga adzafuula mosangalala chifukwa chokhala ndi chimwemwe mumtima,
Koma inu mudzalira chifukwa chopwetekedwa mtima
Ndipo mudzalira mofuula chifukwa chosweka mtima.
15 Inu mudzasiya dzina limene anthu anga osankhidwa azidzagwiritsa ntchito potemberera
Ndipo Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, adzapha aliyense wa inu,
Koma atumiki ake adzawapatsa dzina lina,+
16 Moti aliyense wofuna kudalitsidwa padziko lapansi
Adzadalitsidwa ndi Mulungu amene amanena zoona,*
Ndipo aliyense wochita lumbiro padziko lapansi
Chifukwa mavuto akale adzaiwalika
Adzabisidwa kuti ndisawaonenso.+
17 Taonani! Ndikulenga kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano.+
Ndipo zinthu zakale sizidzakumbukiridwanso,
Kapena kuvutitsa maganizo.+
18 Choncho kondwerani ndipo muzisangalala mpaka kalekale ndi zimene ndikulenga.
Chifukwa ndikulenga Yerusalemu kuti akhale chinthu chosangalatsa
Ndiponso anthu ake kuti akhale chinthu chokondweretsa.+
19 Ndidzasangalala ndi Yerusalemu ndipo ndidzakondwera ndi anthu anga.+
Mwa iye simudzamvekanso phokoso losonyeza kuti munthu akulira kapena kulira chifukwa cha mavuto.”+
20 “Kumeneko sikudzakhalanso mwana wakhanda amene adzangokhala ndi moyo masiku ochepa okha,
Kapena munthu wachikulire amene sadzakwanitsa zaka zimene munthu amafunika kukhala ndi moyo.
Chifukwa aliyense amene adzamwalire ali ndi zaka 100 adzaonedwa ngati kamnyamata,
Ndipo wochimwa adzatembereredwa, ngakhale atakhala ndi zaka 100.*
22 Sadzamanga nyumba kuti wina azikhalamo,
Kapena kudzala kuti ena adye.
Chifukwa masiku a anthu anga adzakhala ngati masiku a mtengo,+
Ndipo anthu anga osankhidwa adzasangalala mokwanira ndi ntchito ya manja awo.
23 Sadzagwira ntchito mwakhama pachabe,+
Kapena kubereka ana kuti akumane ndi mavuto,
Chifukwa iwo ndiponso ana awo+
24 Iwo asanandiitane, ine ndidzayankha.
Asanamalize kulankhula, ine ndidzamva.
25 Mmbulu ndi mwana wa nkhosa zidzadyera pamodzi,
Mkango udzadya udzu ngati ngʼombe yamphongo,+
Ndipo chakudya cha njoka chidzakhala fumbi.
Zimenezi sizidzapweteka aliyense kapena kuwononga chilichonse mʼphiri langa lonse loyera,”+ akutero Yehova.
66 Yehova wanena kuti:
“Kumwamba ndi mpando wanga wachifumu ndipo dziko lapansi ndi chopondapo mapazi anga.+
2 “Dzanja langa ndi limene linapanga zinthu zonsezi,
Ndipo izi ndi zimene zinachitika kuti zonsezi zikhalepo,” akutero Yehova.+
“Choncho ine ndidzayangʼana munthu ameneyu,
Ndidzayangʼana munthu wodzichepetsa ndiponso wosweka mtima amene amadera nkhawa mawu anga.+
3 Munthu amene akupha ngʼombe yamphongo ali ngati amene akupha munthu.+
Amene akupereka nsembe ya nkhosa ali ngati amene akuthyola khosi la galu.+
Munthu amene akupereka mphatso ali ngati amene akupereka magazi a nkhumba.+
Amene akupereka nsembe yachikumbutso ya lubani+ ali ngati munthu amene akupereka dalitso pogwiritsa ntchito mawu onenerera zamatsenga.*+
Anthuwo asankha njira zawozawo,
Ndipo amasangalala ndi zinthu zonyansa.
4 Choncho ndidzasankha njira zowalangira,+
Ndipo ndidzawabweretsera zinthu zimene amachita nazo mantha.
Chifukwa nditaitana, palibe amene anayankha.
Nditalankhula, palibe amene anamvetsera.+
Iwo anapitiriza kuchita zinthu zoipa pamaso panga
Ndipo anasankha kuchita zinthu zimene sizinandisangalatse.”+
5 Imvani mawu a Yehova, inu amene mumadera nkhawa mawu ake:
“Abale anu amene akudana nanu ndipo amakusalani chifukwa cha dzina langa anati, ‘Alemekezeke Yehova!’+
Koma Mulungu adzaonekera nʼkukuchititsani kuti musangalale,
Ndipo iwowo ndi amene adzachititsidwe manyazi.”+
6 Mumzinda mukumveka phokoso lachipwirikiti, phokoso lochokera kukachisi.
Limeneli ndi phokoso losonyeza kuti Yehova akubwezera adani ake chilango chowayenerera.
7 Mkazi anabereka asanayambe kumva zowawa za pobereka.+
Asanayambe kumva ululu wa pobereka, iye anabereka mwana wamwamuna.
8 Ndi ndani anamvapo zinthu ngati zimenezi?
Ndi ndani anaonapo zinthu zoterezi?
Kodi dziko lingabadwe tsiku limodzi?
Kapena kodi mtundu wa anthu ungabadwe nthawi imodzi?
Koma Ziyoni atangoyamba kumva zowawa za pobereka, anabereka ana aamuna.
9 “Kodi ine ndingachititse kuti mwana atsale pangʼono kubadwa koma nʼkumulepheretsa kuti abadwe?” akutero Yehova.
“Kapena kodi ndingachititse kuti mwana ayambe kubadwa kenako nʼkutseka chiberekero?” akutero Mulungu wanu.
10 Sangalalani ndi Yerusalemu ndipo kondwerani naye,+ inu nonse amene mumamukonda.+
Sangalalani naye kwambiri, inu nonse amene mukumulirira,
11 Chifukwa mudzayamwa bere lake lotonthoza ndipo mudzakhuta kwambiri,
Komanso mudzamwa mkaka wake mokwanira ndipo mudzasangalala kwambiri ndi ulemerero wake.
12 Chifukwa Yehova wanena kuti:
“Ndikumupatsa mtendere ngati mtsinje+
Komanso ulemerero wa mitundu ya anthu ngati mtsinje wosefukira.+
Inu mudzayamwa komanso adzakunyamulani mʼmanja,
Ndipo adzakudumphitsani pamiyendo.
13 Mofanana ndi mayi amene amatonthoza mwana wake,
Inenso ndidzapitiriza kukutonthozani.+
Ndipo mudzatonthozedwa chifukwa cha Yerusalemu.+
14 Mudzaona zimenezi ndipo mtima wanu udzasangalala.
Mafupa anu adzakhala ndi mphamvu ngati udzu wobiriwira.
15 “Chifukwa Yehova adzabwera ngati moto,+
Ndipo magaleta ake ali ngati mphepo yamkuntho,+
Kuti adzawabwezere atakwiya kwambiri,
Ndiponso kuti adzawadzudzule ndi malawi a moto.+
16 Yehova adzapereka chiweruzo pogwiritsa ntchito moto,
Inde adzagwiritsa ntchito lupanga lake poweruza anthu onse,
Ndipo anthu ophedwa ndi Yehova adzakhala ambiri.
17 Anthu amene akudzipatula nʼkudziyeretsa potsatira fano limene lili pakati pa mundawo,*+ amene akudya nyama ya nkhumba,+ zinthu zonyansa komanso mbewa,+ onsewo adzathera limodzi,” akutero Yehova. 18 “Popeza ndikudziwa ntchito zawo ndi maganizo awo, ine ndikubwera kudzasonkhanitsa pamodzi anthu a mitundu yonse ndi zilankhulo zonse ndipo iwo adzabwera nʼkuona ulemerero wanga.
19 Ndidzaika chizindikiro pakati pawo ndipo ena mwa anthu amene adzapulumuke ndidzawatumiza ku mitundu ya anthu. Ndidzawatumiza kwa anthu aluso lokoka uta omwe ndi a ku Tarisi,+ ku Puli ndi ku Ludi.+ Ndidzawatumizanso kwa anthu a ku Tubala ndi ku Yavani+ komanso akuzilumba zakutali amene sanamvepo zokhudza ine kapena kuona ulemerero wanga. Iwo adzalengeza za ulemerero wanga pakati pa mitundu ya anthu.+ 20 Adzabweretsa abale anu onse kuchokera ku mitundu yonse+ ngati mphatso kwa Yehova. Adzawabweretsa atakwera mahatchi, ngolo, ngolo zotseka pamwamba, nyulu* ndi ngamila zothamanga, mpaka kukafika kuphiri langa loyera, ku Yerusalemu. Adzachita zimenezi ngati mmene Aisiraeli amabweretsera mphatso mʼnyumba ya Yehova, ataiika mʼchiwiya choyera,” akutero Yehova.
21 “Ndidzatenganso anthu ena kuti akhale ansembe ndi Alevi,” akutero Yehova.
22 “Chifukwa kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano+ zimene ndikupanga zidzapitiriza kukhala pamaso panga. Mofanana ndi zimenezi, ana anu* ndi dzina lanu zidzapitiriza kukhalapo,”+ akutero Yehova.
23 “Kuyambira tsiku limene mwezi watsopano waoneka mpaka tsiku limene mwezi wina watsopano udzaoneke ndiponso sabata lililonse,
Anthu onse adzabwera kudzagwada* pamaso panga,”+ akutero Yehova.
24 “Iwo adzapita kukaona mitembo ya anthu amene anandipandukira.
Chifukwa mphutsi zodya mitemboyo sizidzafa.
Komanso moto umene ukuiwotcha sudzazimitsidwa,+
Ndipo idzakhala chinthu chonyansa kwa anthu onse.”
Kutanthauza kuti, “Chipulumutso cha Yehova.”
Kapena kuti, “sakudziwa mbuye wawo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “sizinafinyidwe.”
Mawu akuti “mwana wamkazi wa Ziyoni” ndi mawu a ndakatulo ndipo nthawi zambiri amanena za mzinda wa Yerusalemu kapena anthu amene ankakhala mumzindawo.
Ena amati “khumbi,” kapena “chitala.”
Kapena kuti, “malangizo.”
Zimenezi ndi zonyansa zotsalira poyenga zitsulo.
Kapena kuti, “mowa wamasese.”
Zikuoneka kuti imeneyi ndi mitengo komanso minda imene ankaigwiritsa ntchito polambira mafano.
Kapena kuti, “malangizo adzaphunzitsidwa.”
Ena amati suntche.
Kapena kuti, “osachedwa kusintha maganizo.”
Kapena kuti, “wochiritsa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼmaso ake olemekezeka.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “adzadya zipatso za zochita zawo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “atasolola makosi awo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “nyumba zimene mumakhala moyo.”
Kapena kuti, “zigoba zodzikongoletsera.”
Chimenechi ndi chizindikiro chimene ankachiika pathupi la kapolo kapena mkaidi.
Amenewa ndi manyazi omwe munthu amakhala nawo chifukwa choti sanakwatiwe komanso alibe ana.
Mʼchilankhulo choyambirira, “ndowe.”
Zikuoneka kuti amenewa anali malo aakulu pafupifupi mahekitala 4.
Onani Zakumapeto B14.
Onani Zakumapeto B14.
Onani Zakumapeto B14.
Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Kapena kuti, “chilungamo chake.”
Kapena kuti, “Chosankha.”
Kapena kuti, “malangizo.”
Kapena kuti, “ndi okonzekera kuponya mivi.”
Kapena kuti, “mikango yamphamvu yamanyenje.”
Kapena kuti, “mbadwa.”
Kutanthauza, “Otsalira Okha Adzabwerera.”
Kapena kuti, “Tikagumule mipanda yake.” Mʼchilankhulo choyambirira, “Tikalibowole.”
Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Kapena kuti, “Namwali.”
Kutanthauza, “Mulungu Ali Nafe.”
Bata ndi chakudya chopangidwa kuchokera ku mkaka.
Kapena kuti, “mʼmakhwawa okhala.”
Umenewu ndi mtsinje wa Firate.
Mʼchilankhulo choyambirira, “cholembera cha munthu wochokera kufumbi.”
Dzina limeneli likusonyeza kuti anthu adzabwera mofulumira kudzalanda dziko la adani.
Kapena kuti, “zichitire umboni.”
Ameneyu anali mkazi wa Yesaya.
Silowa inali ngalande ya madzi.
Umenewu ndi mtsinje wa Firate.
Onani Yes. 7:14.
MʼChiheberi mawu akuti “Mulungu ali nafe” ndi tanthauzo la dzina lakuti Emanueli. Onani Yes. 7:14; 8:8.
Kapena kuti, “umboni wotsimikizira zimenezi.”
Kapena kuti, “malangizo.”
Kapena kuti, “kuyembekezera mwachidwi.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “sadzaona mʼmbandakucha.”
Kapena kuti, “boma; ulamuliro wa kalonga.”
Kapena kuti, “Boma; Ulamuliro wa kalonga.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “adzachokera kumbuyo.”
Mabaibulo ena amati, “nthambi ya kanjedza ndi bango.”
Kapena kuti, “lachilango.”
Kapena kuti, “ulemerero.”
Kutanthauza “Msuri” amene watchulidwa pavesi 5 ndi 24.
Mawu akuti “mwana wamkazi wa Ziyoni” ndi mawu a ndakatulo ndipo nthawi zambiri amanena za mzinda wa Yerusalemu kapena anthu amene ankakhala mumzindawo.
Kapena kuti, “mzimu.”
Mabaibulo ena amati, “zidzadyera limodzi.”
Kapena kuti, “Anthu a mitundu ina adzamufunafuna.”
Ameneyu ndi Babeloniya.
Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼmapewa a.”
Kapena kuti, “adzasonyeza mphamvu zawo pa.”
Mabaibulo ena amati, “adzaphwetsa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “lilime la.”
Umenewu ndi mtsinje wa Firate.
Kapena kuti, “mzimu.”
Mabaibulo ena amati, “adzaugawa mtsinjewo kukhala timitsinje tisanu ndi tiwiri.”
“Ya” ndi chidule cha dzina lakuti Yehova.
Mʼchilankhulo choyambirira, “iwe mkazi wokhala mu Ziyoni.” Apa anthu onse okhala mu Ziyoni akuwatenga ngati mkazi.
Mʼchilankhulo choyambirira, “kwa anthu anga opatulika.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ndi makesili awo,” mwina kutanthauza mlalangʼamba wa Oriyoni ndi milalangʼamba ina imene uli nayo pafupi.
Kapena kuti, “yemwe ndi chokongoletsera maufumu.”
Mabaibulo ena amati, “ziwanda zooneka ngati mbuzi.”
Kapena kuti, “adzawapatsa mpumulo.”
Mtengo wa junipa ndi wofanana ndi mtengo wa mkungudza.
Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mʼchilankhulo choyambirira, “atonde.”
Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼnyumba.”
Kapena kuti, “nthambi.”
“Nungu” ndi nyama yamʼtchire yomwe ili ndi minga zodzitetezera thupi lonse.
Kapena kuti, “dzanja lakonzekera.”
Kapena kuti, “njoka yapoizoni yothamanga kwambiri.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “muzu wako.”
Kapena kuti, “khwawa.”
Mawu akuti “mwana wamkazi wa Ziyoni” ndi mawu a ndakatulo ndipo nthawi zambiri amanena za mzinda wa Yerusalemu kapena anthu amene ankakhala mumzindawo.
Kapena kuti, “zodzaza ndi mphesa zakupsa.”
Mabaibulo ena amati, “Chifukwa chakuti kufuula kwa anthu omenya nkhondo kwamveka pa zipatso za mʼchilimwe komanso zokolola zako.”
Kapena kuti, “zimene zidzawerengedwe mosamala kwambiri ngati mmene munthu waganyu amachitira,” kutanthauza ndendende zaka zitatu.
Mʼchilankhulo choyambirira, “ana a Isiraeli.”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Kapena kuti, “yosangalatsa.”
Kapena kuti, “mulungu wachilendo.”
“Mankhusu” ndi makoko amene amachotsa kumbewu ngati mpunga popuntha ndipo amatha kuwauluza ndi mphepo.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mabaibulo ena amati, “nʼkumayangʼana ndili pamalo anga okhala.”
“Mlulu” ndi zomera zitalizitali zimene zimakonda kumera mʼmadambo.
“Fulakesi” ndi mbewu imene ankalima ku Iguputo ndipo ankaigwiritsa ntchito popanga ulusi wowombera nsalu.
Mʼchilankhulo choyambirira, “anthu owomba nsalu pogwiritsa ntchito chowombela nsalu.”
Kapena kuti, “Memfisi.”
Mabaibulo ena amati, “nthambi ya kanjedza kapena bango.”
Kapena kuti, “mkulu wa asilikali.”
Kapena kuti, “nʼkumayenda asanavale mokwanira.”
Kapena kuti, “amene ankasirira kukongola kwake.”
Zikuoneka kuti akunena za chigawo cha Babeloniya wakale.
Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼchiuno mwanga mwadzaza ululu woopsa.”
Kapena kuti, “thirani mafuta.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Mwana wamwamuna wapamalo.”
Kutanthauza, “Kukhala Chete.”
Zikuoneka kuti akunena chipululu cha Arabiya.
Kapena kuti, “zimene zidzawerengedwe mosamala kwambiri ngati mmene munthu waganyu amachitira,” kutanthauza ndendende chaka chimodzi.
Zikuoneka kuti akunena za Yerusalemu.
Kapena kuti, “anakonza.”
Kapena kuti, “Chitetezo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “malo okhala.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “kulemera.”
Kapena kuti, “mphukira.”
Umenewu ndi mtsinje wotuluka mumtsinje wa Nailo.
Mʼchilankhulo choyambirira, “anamwali.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ndi masiku a.”
Kapena kuti, “wagadabuza.”
Mabaibulo ena amati, “lauma.”
Kapena kuti, “pangano lakalekale.”
Mabaibulo ena amati, “wauma.”
Kapena kuti, “kumadzulo.”
Kapena kuti, “kumʼmawa.”
Ena amati “khumbi,” kapena “chitala.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “achikulire ake.”
Kapena kuti, “vinyo yemwe nsenga zake zadikha pansi chifukwa chokhalitsa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “adzameza.”
Kapena kuti, “adzathetsa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “lidzakhazikika pa.”
Mabaibulo ena amati, “Anthu a mtima wokhazikika.”
“Ya” ndi chidule cha dzina lakuti Yehova.
Kapena kuti, “ndi yosalazika.”
Kutanthauza, Mulungu ndi dzina lake akumbukiridwe, anthu amudziwe.
Mʼchilankhulo choyambirira, “adzaona mmene mukudziperekera chifukwa cha anthu anu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Mtembo wanga udzadzuka.”
Mabaibulo ena amati, “ali ngati mame a maluwa.”
Kapena kuti, “lidzabereka anthu amene anafa.”
Kapena kuti, “chilango chitadutsa.”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Zikuoneka kuti mkazi ameneyu akunena Isiraeli ndipo akumuyerekezera ndi munda wampesa.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Umenewu ndi mtsinje wa Firate.
Zikuoneka kuti akunena mzinda wa Samariya, womwe ndi likulu la dzikoli.
Kapena kuti, “chodzikuza; chonyada.”
Kapena kuti, “zodzikuza; zonyada.”
Kapena kuti, “Chingwe choyezera pachingwe choyezera, chingwe choyezera pachingwe choyezera.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mulomo wachibwibwi.”
Kapena kuti, “Chingwe choyezera pachingwe choyezera, chingwe choyezera pachingwe choyezera.”
Mabaibulo ena amati, “taona masomphenya limodzi.”
Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Chimenechi ndi chipangizo chimene amachigwiritsa ntchito pofuna kuonetsetsa kuti pamalo pakhale pa fulati.
Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mabaibulo ena amati, “Anthu akadzamvetsetsa uthenga umenewu adzachita mantha kwambiri.”
Kapena kuti, “dziko lonse lapansi.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “komanso sipeloti.” Sipeloti ndi mtundu wa tirigu koma wosakoma ngati tirigu weniweni.
Kapena kuti, “amalanga; amakwapula.”
Kapena kuti, “Amene nzeru zake nʼzazikulu.”
Mwina akutanthauza, “Malo Osonkhapo Moto a Paguwa Lansembe la Mulungu.” Zikuoneka kuti akunena za Yerusalemu.
Kapena kuti, “anthu achilendo.”
Kapena kuti, “zolinga zawo zoipa.”
Kapena kuti, “Ndinu opotoka maganizo kwambiri.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “amene akudzudzula.”
Kutanthauza, chifukwa cha manyazi ndiponso kukhumudwa.
Mʼchilankhulo choyambirira, “amathira pansi chakumwa ngati nsembe.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “malo otetezeka a Farao.”
Kapena kuti, “njoka yapoizoni yothamanga kwambiri.”
Kapena kuti, “malangizo.”
Mabaibulo ena amati, “pachitsime.”
Kapena kuti, “mafano anu achitsulo chosungunula.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “chamafuta komanso chonona.”
Kapena kuti, “mafupa othyoka.”
Kapena kuti, “Mpweya.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “sefa wa zinthu zopanda pake.”
Kapena kuti, “Pamene mukudziyeretsa kuti muchite.”
Kapena kuti, “akumvetsera kulira kwa.”
Palembali mawu akuti “Tofeti” agwiritsidwa ntchito mophiphiritsa monga malo oyaka moto, ndipo akuimira chiwonongeko.
Kapena kuti, “anthu okwera pamahatchi.”
Kapena kuti, “moto wake uli mu Ziyoni.”
Kapena kuti, “malo othawirapo.”
Kapena kuti, “kuti achite zinthu zosayenera.”
Apa akunena mdani.
Mabaibulo ena amati, “lauma.”
Kapena kuti, “malo okwezeka achitetezo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “nʼchozama.”
Kapena kuti, “Magazi awo adzayenda mʼmapiri.”
Zikuoneka kuti akunena Bozira, likulu la Edomu.
Mabaibulo ena amati, “chiwanda chooneka ngati mbuzi chidzaitana chinzake.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “lawagawira malowo ndi chingwe choyezera.”
Kapena kuti, “lidzachita maluwa ngati safironi.”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Kapena kuti “mkulu wa operekera zakumwa.”
Kapena kuti, “mʼchilankhulo cha Asiriya.”
Kapena kuti, “nyumba yachifumu.”
Kapena kuti, “nyumba yachifumu.”
Kapena kuti, “kunyoza.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Zili ngati ana afika pakhomo la chiberekero.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mzimu.”
Mabaibulo ena amati, “pakati.”
Mawu akuti “mwana wamkazi wa Ziyoni” ndi mawu a ndakatulo ndipo nthawi zambiri amanena za mzinda wa Yerusalemu kapena anthu amene ankakhala mumzindawo.
Mawu akuti “mwana wamkazi wa Yerusalemu” ndi mawu a ndakatulo ndipo nthawi zambiri amanena za mzinda wa Yerusalemu kapena anthu amene ankakhala mumzindawo.
Mtengo wa junipa ndi wofanana ndi mtengo wa mkungudza.
Kapena kuti, “ngalande za mtsinje wa Nailo.”
Kutanthauza chizindikiro cha Hezekiya.
Mʼchilankhulo choyambirira, “masiku ako.”
Nʼkutheka kuti masitepe amenewa ankawagwiritsa ntchito ngati chipangizo chodziwira nthawi.
Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
“Ya” ndi chidule cha dzina lakuti Yehova.
Kapena kuti, “kupwetekedwa moyo.”
Kutanthauza mawu a Mulungu ndi zochita zake.
Kapena kuti, “Mwachotsa machimo anga onse kuti musawaonenso.”
Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mʼchilankhulo choyambirira, “anasangalala.”
Kapena kuti, “nyumba yachifumu.”
Kapena kuti, “choonadi.”
Kapena kuti, “momutonthoza.”
Kapena kuti, “walandira kuwirikiza kawiri.”
Kapena kuti, “mzimu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mkono.”
Kapena kuti, “adzaweta.”
Mabaibulo ena amati, “anamvetsa.”
Kapena kuti, “singakhale nkhuni zokwanira.”
Kapena kuti, “chifaniziro chopangidwa ndi chitsulo chosungunula.”
Kapena kuti, “olamulira.”
Kapena kuti, “angayeze.”
Kapena kuti, “khalani chete pamaso panga.”
Kapena kuti, “kuchokera kumʼmawa.”
Kutanthauza kumutumikira.
Mʼchilankhulo choyambirira, “Mbewu.”
Kutanthauza wopanda chitetezo chilichonse komanso wonyozeka.
Mtengo wa junipa ndi wofanana ndi mtengo wa mkungudza.
Umenewu ndi mtengo waukulu umene umatalika mpaka mamita 15. Umakhala ndi masamba osabiriwira kwambiri ndi nthambi zotuwa ngati phulusa.
Mʼchilankhulo choyambirira, “zoyambirira.”
Kapena kuti, “kuchokera kumʼmawa.”
Kapena kuti, “achiwiri kwa olamulira.”
Kapena kuti, “ndi chinthu chimene kulibe.”
Kapena kuti, “zitsulo zosungunula.”
Kapena kuti, “malangizo ake.”
Kapena kuti, “mphamvu ya moyo.”
Kapena kuti, “mayiko amʼmbali mwa nyanja.”
Kapena kuti, “zifaniziro zopangidwa ndi zitsulo zosungunula.”
Kapena kuti, “malangizo.”
Kapena kuti, “malangizo.”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”
Kapena kuti, “kundidalira.”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Chimenechi ndi chomera chonunkhira. Mtundu weniweni wa chomerachi sukudziwika.
Kapena kuti, “zochita zako zondipandukira.”
Nʼkutheka kuti akunena aphunzitsi a Chilamulo.
Kapena kuti, “kuyambira usanabadwe.”
Kutanthauza “Wolungama.” Limeneli ndi dzina laulemu la Isiraeli.
Kapena kuti, “dziko laludzu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu yako.”
Kapena kuti, “kapena chifaniziro chopangidwa ndi chitsulo chosungunula.”
Ena amati kasemasema.
Kapena kuti, “mʼkachisi.”
Kapena kuti, “mtengo woumawu?”
Kapena kuti, “za aneneri abodza.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ndimasule mʼchiuno mwa mafumu.”
Kapena kuti, “zamkuwa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Ndidzakumanga mwamphamvu mʼchiuno mwako.”
Kapena kuti, “Kuchokera kumʼmawa kukafika kumadzulo.”
Kapena kuti, “akutsutsana.”
Kapena kuti, “amene akuliumba.”
Mabaibulo ena amati, “Kapena kodi dongo linganene kuti: ‘Chimene waumbacho chilibe zogwiriraʼ?”
Kapena kuti, “Mukuvutikiranji ndi ululu wa pobereka.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “magulu awo onse ankhondo.”
Mabaibulo ena amati, “Antchito a ku Iguputo.”
Mabaibulo ena amati, “amalonda.”
Mabaibulo ena amati, “sanalipange kuti likhale lopanda kanthu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”
Katundu ameneyu ndi mafano amene anyamulitsa nyama.
Mʼchilankhulo choyambirira, “kumugwadira.”
Kapena kuti, “kumʼmawa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “a mtima wamphamvu.”
Mawu akuti “mwana wamkazi wa Babulo” ndi mawu a ndakatulo ndipo nthawi zambiri amanena za mzinda wa Babulo kapena anthu amene ankakhala mumzindawo.
Mabaibulo ena amati, “amene ndidzamusonyeze chifundo.”
Kapena kuti, “Mfumukazi.”
Kapena kuti, “Mfumukazi.”
Mabaibulo ena amati, “Ngakhale.”
Kapena kuti, “Ndipo sudzatha kulichitira matsenga kuti lisakugwere.”
Mabaibulo ena amati, “Anthu okhulupirira nyenyezi.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “chigawo chake.”
Mabaibulo ena amati, “amene ndinu a fuko la Yuda.”
Kapena kuti, “mkuwa.”
Kapena kuti, “chifaniziro chopangidwa ndi chitsulo chosungunula.”
Mabaibulo ena amati, “ndinakusankhani.”
Kapena kuti, “Sindigawana ulemerero wanga ndi wina aliyense.”
Kapena kuti, “limodzi ndi.”
Kapena kuti, “ndimakuphunzitsani chifukwa cha ubwino wanu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Mbewu zanu zidzachuluka.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ndili mʼmimba.”
Kapena kuti, “Yehova adzandichitira chilungamo.”
Kapena kuti, “mphoto yanga.”
Mabaibulo ena amati, “Ndipo mʼmapiri onse opanda kanthu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “pachifuwa.”
Kapena kuti, “lilime lophunzitsidwa bwino.”
Mabaibulo ena amati, “ndingalimbikitsire.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Amadzutsa khutu langa kuti limvetsere.”
Kapena kuti, “angalimbane nane pa.”
Mawu a Chiheberi amene amasuliridwa kuti “njenjete” amatanthauza mtundu winawake wa kadziwotche amene amadya zovala.
Kapena kuti, “amene anakuberekani ndi zowawa zapobereka.”
Kapena kuti, “mphamvu zanga.”
Kapena kuti, “sichidzaphwanyika.”
Kapena kuti, “malangizo anga ali.”
Mawu a Chiheberi amene amasuliridwa kuti “njenjete” amatanthauza mtundu winawake wa kadziwotche amene amadya zovala.
Mabaibulo ena amati, “mbozi zodya zovala zidzawadya.”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mawu akuti “mwana wamkazi wa Ziyoni” ndi mawu a ndakatulo ndipo nthawi zambiri amanena za mzinda wa Yerusalemu kapena anthu amene ankakhala mumzindawo.
Kapena kuti, “wachita kuti tipambane.”
Kapena kuti, “adzasowa chonena.”
Mabaibulo ena amati, “zimene ife tinamva.”
“Winawake” angaimire munthu wina amene akungoonerera kapena Mulungu.
Kapena kuti, “saoneka mwapadera moti nʼkumusirira.”
Kapena kuti, “amene ankamvetsa kuti kupweteka nʼchiyani.”
Mabaibulo ena amati, “Anali ngati munthu amene anzake amaphimba nkhope zawo akamuona.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “amene wakwapulidwa.”
Kapena kuti, “wa zochitika pa moyo wake.”
Kapena kuti, “anamenyedwa mpaka kufa.”
Kapena kuti, “Ndipo wina adzapereka manda ake.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “munthu wolemera.”
Kapena kuti, “sanachite zachiwawa.”
Kapena kuti, “Koma zinamukomera Yehova.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu zake.”
Kapena kuti, “zimene zimasangalatsa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “anakhuthula moyo wake mu imfa.”
Kapena kuti, “ali ndi mbuye.”
Kapena kuti, “ali ngati mbuye.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “wopwetekedwa mtima.”
Kapena kuti, “miyala yofiira ngati moto.”
Kapena kuti, “ndalama zimene mumazipeza movutikira.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “zamafuta.”
Kapena kuti, “chipale chofewa.”
Mtengo wa junipa ndi wofanana ndi mtengo wa mkungudza.
Kapena kuti, “zidzamupangira dzina.”
Mabaibulo ena amati, “Ndipo tsoka wasiyana nalo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “pabedi.”
Kapena kuti, “mʼmakhwawa.”
Kapena kuti, “mʼkhwawa.”
Kapena kuti, “ndidzitonthoze.”
Nʼkutheka kuti akunena za kulambira mafano.
Mabaibulo ena amati, “mfumu.”
Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mʼchilankhulo choyambirira, “sunatope.”
Kapena kuti, “zokusangalatsani.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ndi zibakera zoipa.”
Kapena kuti, “zimene mtima wanu umalakalaka.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mukubweza phazi lanu.”
Kapena kuti, “zokusangalatsani.”
Kapena kuti, “musangalale.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “si lolemera.”
Kapena kuti, “kuona mtima kwapunthwa.”
Kapena kuti, “Kuona mtima kwasowa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ndipo zinamuipira mʼmaso mwake.”
Kapena kuti, “anawachititsa kuti apambane.”
Kapena kuti, “cha kupambana.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu zako.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu ya mbewu yako.”
Kapena kuti, “kuwala kwa mʼbandakucha wako.”
Kapena kuti, “nyumba yanga yokongola.”
Kapena kuti, “kumakomo a makola awo.”
Kapena kuti, “adzakukongoletsa.”
Kapena kuti, “chifukwa chokufunira zabwino.”
Mtengo wa junipa ndi wofanana ndi mtengo wa mkungudza.
Umenewu ndi mtengo waukulu umene umatalika mpaka mamita 15. Umakhala ndi masamba osabiriwira kwambiri ndi nthambi zotuwa ngati phulusa.
Kapena kuti, “mkuwa.”
Kapena kuti, “chofunira anthu zabwino.”
Kapena kuti, “aoneke kukongola.”
Kapena kuti, “cha chuma chimene.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Mbewu zawo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu zimene.”
Kapena kuti, “malaya odula manja a chilungamo.”
Kapena kuti, “pakamwa pa Yehova padzasankhe.”
Mawu akuti “mwana wamkazi wa Ziyoni” ndi mawu a ndakatulo ndipo nthawi zambiri amanena za mzinda wa Yerusalemu kapena anthu amene ankakhala mumzindawo.
Mabaibulo ena amati, “zovala zofiira kwambiri.”
Kapena kuti, “linandithandiza kuti ndipambane.”
Kapena kuti, “zachinyengo.”
Kapena kuti, “mngelo amene amaonekera pamaso pake.”
Kapena kuti, “madzi akuya.”
Kapena kuti, “mʼchigwa.”
Kapena kuti, “lokongola.”
Kapena kuti, “okongola.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “kubwadamuka kwa mʼmimba mwanu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “tisungunuke.”
Kapena kuti, “amene munatipanga.”
Kapena kuti, “Kachisi wathu woyera.”
Kapena kuti, “yokongola.”
Mabaibulo ena amati, “amakhala mʼzisimba.”
Mabaibulo ena amati, “Chifukwa ungatengere kupatulika kwanga.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ndipo ndiika chilangocho pachifuwa pawo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “nʼkuwaika pachifuwa pawo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “dalitso.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”
Kapena kuti, “amene ndi wokhulupirika.” Mʼchilankhulo choyambirira, “Ame.”
Kapena kuti, “amene ndi wokhulupirika.” Mʼchilankhulo choyambirira, “Ame.”
Mabaibulo ena amati, “Amene adzalephere kufika zaka 100 adzatengedwa kukhala wotembereredwa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”
Mabaibulo ena amati, “amene amapembedza fano.”
Kapena kuti, “mphamvu za.”
Umenewu ndi munda wapadera umene ankaugwiritsa ntchito polambira mafano.
“Nyulu” ndi nyama yooneka ngati hatchi.
Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu zanu.”
Kapena kuti, “kudzalambira.”