Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • nwt Psalms 1:1-150:6
  • Masalimo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Masalimo
  • Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Masalimo

MASALIMO*

BUKU LOYAMBA

(Masalimo 1-41)

1 Wosangalala ndi munthu amene sayenda motsatira malangizo a anthu oipa,

Saima mʼnjira ya anthu ochimwa,+

Ndipo sakhala pansi pamodzi ndi anthu onyoza.+

 2 Koma amakonda kwambiri chilamulo cha Yehova,+

Ndipo amawerenga ndi kuganizira mozama* chilamulocho masana ndi usiku.+

 3 Iye adzakhala ngati mtengo wodzalidwa mʼmbali mwa ngalande za madzi,

Umene umabereka zipatso mʼnyengo yake,

Umenenso masamba ake safota.

Ndipo zonse zimene amachita zimamuyendera bwino.+

 4 Koma si mmene oipa alili.

Iwo ali ngati mankhusu* amene amauluzika ndi mphepo.

 5 Nʼchifukwa chake oipa sadzalephera kulangidwa,+

Ndipo ochimwa sadzapezekanso pamene pali olungama.+

 6 Chifukwa Yehova amadziwa zochita za olungama,+

Koma oipa adzawonongedwa pamodzi ndi zochita zawo.+

2 Nʼchifukwa chiyani anthu a mitundu ina akuchita zipolowe,

Ndiponso nʼchifukwa chiyani mitundu ya anthu ikungʼungʼudza za chinthu chopanda pake?*+

 2 Mafumu a dziko lapansi aima pamalo awo,

Ndipo anthu olemekezeka asonkhana pamodzi* mogwirizana+

Kuti alimbane ndi Yehova komanso wodzozedwa wake.*+

 3 Iwo akunena kuti: “Tiyeni tidule zomangira zawo,

Ndipo titaye zingwe zawo!”

 4 Amene wakhala pampando wachifumu kumwamba adzaseka.

Yehova adzawanyogodola.

 5 Pa nthawiyo, adzalankhula nawo atakwiya,

Ndipo adzawachititsa mantha ndi mkwiyo wake.

 6 Iye adzawauza kuti: “Inetu ndasankha mfumu yanga+

Ndipo ikulamulira ku Ziyoni,+ phiri langa lopatulika.”

 7 Ndifotokoza zimene Yehova wanena.

Iye wandiuza kuti: “Iwe ndiwe mwana wanga,+

Lero, ine ndakhala bambo ako.+

 8 Tandipempha, ndipo ndikupatsa mitundu ya anthu kuti ikhale cholowa chako,

Ndiponso dziko lonse lapansi kuti likhale lako.+

 9 Mitunduyo udzaiphwanya ndi ndodo yachifumu yachitsulo,+

Ndipo udzaiswa ngati chiwiya chadothi.”+

10 Tsopano inu mafumu, sonyezani kuzindikira,

Mverani malangizo,* inu oweruza a dziko lapansi.

11 Tumikirani Yehova mwamantha,

Ndipo muzisangalala komanso kunjenjemera pamaso pake.

12 Mulemekezeni* mwanayo+ kuopera kuti Mulungu angakwiye,

Ndipo mungawonongedwe nʼkuchotsedwa panjira yachilungamo,+

Chifukwa mkwiyo wake umayaka mofulumira.

Osangalala ndi anthu onse amene amathawira kwa iye.

Nyimbo ya Davide pamene ankathawa mwana wake Abisalomu.+

3 Inu Yehova, nʼchifukwa chiyani adani anga achuluka chonchi?+

Nʼchifukwa chiyani anthu ambiri akundiukira?+

 2 Anthu ambiri akunena za ine* kuti:

“Mulungu samupulumutsa ameneyu.”+ (Selah)*

 3 Koma inu Yehova, mumanditeteza mbali zonse+ ngati chishango,

Ndinu ulemerero wanga+ komanso ndinu amene mumatukula mutu wanga.+

 4 Ndidzaitana Yehova mokweza,

Ndipo iye adzandiyankha mʼphiri lake loyera.+ (Selah)

 5 Ine ndidzagona pansi nʼkupeza tulo,

Ndipo ndidzadzuka ndili wotetezeka,

Chifukwa Yehova akupitiriza kundithandiza.+

 6 Sindikuopa anthu masauzandemasauzande

Amene andizungulira kumbali zonse kuti andiukire.+

 7 Nyamukani, inu Yehova! Ndipulumutseni+ inu Mulungu wanga!

Mudzamenya adani anga onse pachibwano.

Mudzaphwanya mano a anthu oipa.+

 8 Chipulumutso chimachokera kwa Yehova.+

Madalitso anu ali pa anthu anu. (Selah)

Kwa wotsogolera nyimbo: Nyimboyi iimbidwe ndi zipangizo za zingwe. Nyimbo ya Davide.

4 Ndikaitana, mundiyankhe inu Mulungu wanga wolungama.+

Mundikonzere njira yoti ndipulumukire* mʼmasautso anga.

Mundikomere mtima ndipo imvani pemphero langa.

 2 Inu ana a anthu, kodi mudzandinyoza mʼmalo mondilemekeza mpaka liti?

Kodi mudzakonda zinthu zopanda pake komanso kufufuza zinthu zoti mundinamizire mpaka liti? (Selah)

 3 Dziwani kuti Yehova adzachita zinthu zapadera kwa munthu amene ndi wokhulupirika kwa iye.*

Yehova adzamva ndikaitana.

 4 Ngati mwakwiya, musachimwe.+

Lankhulani mumtima mwanu muli pabedi panu ndipo mukhale chete. (Selah)

 5 Nsembe iliyonse imene mukupereka kwa Mulungu, muziipereka ndi mtima wabwino,

Ndipo muzikhulupirira Yehova.+

 6 Pali ambiri amene akunena kuti: “Ndi ndani amene adzationetse chinthu chabwino chilichonse?”

Inu Yehova, kuwala kwa nkhope yanu kutiunikire.+

 7 Mwadzaza mtima wanga ndi chisangalalo chachikulu

Kuposa amene ali ndi zokolola zochuluka komanso vinyo watsopano.

 8 Ndidzagona pansi mwamtendere nʼkupeza tulo,+

Chifukwa inu nokha Yehova mumandichititsa kukhala wotetezeka.+

Kwa wotsogolera nyimbo pa Nehiloti.* Nyimbo ya Davide.

5 Mvetserani mawu anga inu Yehova,+

Mvetserani mwatcheru kudandaula kwanga.

 2 Imvani kufuula kwanga kopempha thandizo,

Inu Mfumu yanga komanso Mulungu wanga, chifukwa ndimapemphera kwa inu.

 3 Inu Yehova, mʼmawa mudzamva mawu anga,+

Mʼmawa ndidzafotokoza nkhawa zanga kwa inu+ ndipo ndidzadikira yankho lanu.

 4 Chifukwa inu si Mulungu amene amasangalala ndi zoipa,+

Palibe munthu woipa amene angakhale ndi inu.+

 5 Palibe anthu odzikuza amene angaime pamaso panu.

Mumadana ndi anthu onse amene amachita zoipa.+

 6 Mudzawononga anthu amene amalankhula mabodza.+

Yehova amadana ndi anthu achiwawa komanso achinyengo.*+

 7 Koma ine ndidzalowa mʼnyumba yanu+ chifukwa cha chikondi chanu chachikulu komanso chokhulupirika.+

Ndidzawerama nditayangʼana kumene kuli kachisi wanu wopatulika* chifukwa chokuopani.+

 8 Inu Yehova ndinu wachilungamo,* nditsogolereni chifukwa adani anga andizungulira.

Ndichotsereni zopunthwitsa mʼnjira yanu.+

 9 Chifukwa palibe amene angakhulupirire chilichonse chimene anena.

Mʼmitima yawo muli chidani chokhachokha.

Mmero wawo ndi manda otseguka.

Iwo amalankhula zachinyengo* ndi lilime lawo.+

10 Koma Mulungu adzawapeza ndi mlandu.

Adzagwa chifukwa cha ziwembu zawo zomwe.+

Muwathamangitse chifukwa cha kuchuluka kwa zolakwa zawo,

Chifukwa iwo akupandukirani.

11 Koma anthu onse amene amathawira kwa inu adzasangalala.+

Nthawi zonse adzafuula mosangalala.

Inu mudzawateteza kuti anthu oipa asawafikire,

Ndipo anthu okonda dzina lanu adzasangalala chifukwa cha inu.

12 Chifukwa inu Yehova mudzadalitsa aliyense wolungama.

Mudzasangalala nawo ndipo mudzawateteza ndi chishango chachikulu.+

Kwa wotsogolera nyimbo: Nyimboyi iimbidwe ndi zoimbira za zingwe pa Sheminiti.* Nyimbo ya Davide.

6 Inu Yehova, musandidzudzule mutakwiya,

Musandilangize mutapsa mtima.+

 2 Ndikomereni mtima,* inu Yehova, chifukwa ndayamba kufooka.

Ndichiritseni, inu Yehova,+ chifukwa mafupa anga akunjenjemera.

 3 Ine ndasokonezeka* kwambiri,+

Ndipo ndikufunseni, inu Yehova, kodi ndipitiriza kuvutika mpaka liti?+

 4 Bwererani, inu Yehova, mudzandipulumutse.+

Ndipulumutseni chifukwa cha chikondi chanu chokhulupirika.+

 5 Chifukwa akufa satchula* za inu.

Kodi ndi ndani amene angakutamandeni ali mʼManda?*+

 6 Ndafooka chifukwa cha kuusa moyo kwanga.+

Usiku wonse ndimanyowetsa bedi langa* ndi misozi,

Ndimalira ndipo misozi imadzaza pabedi panga.+

 7 Maso anga afooka chifukwa cha chisoni changa.+

Maso anga achita mdima* chifukwa cha anthu onse amene akundizunza.

 8 Ndichokereni pamaso panga inu nonse amene mumachita zoipa,

Chifukwa Yehova adzamva mawu a kulira kwanga.+

 9 Yehova adzamva pempho langa loti andikomere mtima.+

Yehova adzayankha pemphero langa.

10 Adani anga onse adzachititsidwa manyazi ndipo adzataya mtima.

Iwo adzathawa mwadzidzidzi komanso mwamanyazi.+

Nyimbo yoimba polira imene Davide anaimbira Yehova, yokhudza mawu a Kusi wa fuko la Benjamini.

7 Inu Yehova Mulungu wanga, ine ndathawira kwa inu.+

Ndipulumutseni kwa anthu onse amene akundizunza ndipo mundilanditse.+

 2 Mukapanda kutero andikhadzulakhadzula ngati mmene mkango umachitira,+

Nʼkunditenga popanda wondipulumutsa.

 3 Inu Yehova Mulungu wanga, ngati ndalakwitsa chilichonse,

Ngati ndachita zinthu mopanda chilungamo,

 4 Ngati ndachita zoipa kwa munthu amene akundichitira zabwino,+

Kapena ngati mdani wanga ndamulanda zinthu zake popanda chifukwa,*

 5 Mdani wanga andithamangitse nʼkundipeza,

Andigwetsere pansi nʼkundipondaponda mpaka kufa

Ndipo andisiye nditagona pafumbi mwamanyazi. (Selah)

 6 Nyamukani mutakwiya, inu Yehova.

Imirirani ndi kukhaulitsa adani anga amene andikwiyira.+

Dzukani nʼkundithandiza, ndipo mulamule kuti chilungamo chichitike.+

 7 Mitundu ya anthu ikuzungulireni,

Ndipo inu muwaweruze muli kumwambako.

 8 Yehova adzapereka chigamulo kwa mitundu ya anthu.+

Ndiweruzeni inu Yehova, mogwirizana ndi chilungamo changa

Komanso mogwirizana ndi kukhulupirika kwanga.+

 9 Chonde, thetsani zinthu zoipa zimene anthu oipa akuchita.

Koma muchititse kuti wolungama akhale wolimba,+

Chifukwa inu ndinu Mulungu wolungama+ amene amayeza mitima+ komanso mmene munthu akumvera mumtima.*+

10 Mulungu ndi chishango changa,+ Mpulumutsi wa anthu owongoka mtima.+

11 Mulungu ndi Woweruza wolungama,+

Ndipo Mulungu amapereka zigamulo kwa* oipa tsiku lililonse.

12 Ngati munthu sakulapa,+ Mulungu amanola lupanga lake,+

Amakunga uta wake nʼkukonzekera kulasa.+

13 Iye amakhala wokonzeka kugwiritsa ntchito zida zake zoopsa,

Amakhala wokonzeka kugwiritsa ntchito mivi yake yoyaka moto.+

14 Taonani munthu amene ali ndi pakati pa zinthu zoipa,

Watenga pakati pa mavuto ndipo adzabereka mabodza.+

15 Iye wakumba dzenje ndipo walizamitsa,

Koma adzagwera mʼdzenje limene wakumba yekhalo.+

16 Mavuto amene akuwayambitsawo adzabwerera pamutu pake,+

Zinthu zachiwawa zimene akuchita zidzagwera paliwombo pake.

17 Ndidzatamanda Yehova chifukwa cha chilungamo chake.+

Ndidzaimba nyimbo zotamanda dzina la Yehova+ Wamʼmwambamwamba.+

Kwa wotsogolera nyimbo, pa Gititi.* Nyimbo ya Davide.

8 Inu Yehova Ambuye wathu, dzina lanu ndi lalikulu padziko lonse lapansi,

Mwachititsa kuti ulemerero wanu ukhale pamwamba kuposa kumwamba!+

 2 Kudzera mʼmawu otamanda ochokera mʼkamwa mwa ana ndi mwa makanda+

Mwasonyeza mphamvu zanu chifukwa cha adani anu,

Kuti adani anu komanso amene akufuna kukubwezerani zoipa akhale chete.

 3 Ndikayangʼana kumwamba, ntchito ya zala zanu,

Mwezi ndi nyenyezi zimene munapanga,+

 4 Ndimaganiza kuti, munthu ndi ndani kuti muzimuganizira,

Ndipo mwana wa munthu ndi ndani kuti muzimusamalira?+

 5 Munamutsitsa pangʼono poyerekeza ndi angelo,*

Ndipo munamuveka ulemerero ndi ulemu ngati chisoti chachifumu.

 6 Munamupatsa mphamvu kuti alamulire ntchito za manja anu.+

Mwaika zinthu zonse pansi pa mapazi ake:

 7 Nkhosa, mbuzi ndi ngʼombe zonse,

Komanso nyama zakutchire,*+

 8 Mbalame zamumlengalenga komanso nsomba zamʼnyanja,

Chilichonse chimene chimasambira mʼnyanja.

 9 Inu Yehova Ambuye wathu, dzina lanu ndi lalikulu padziko lonse lapansi!

Kwa wotsogolera nyimbo, pa Mutilabeni.* Nyimbo ya Davide.

א [Aleph]

9 Ndidzakutamandani inu Yehova ndi mtima wanga wonse.

Ndidzafotokoza za ntchito zanu zonse zodabwitsa.+

 2 Ndidzakondwera ndi kusangalala chifukwa cha inu,

Ndidzaimba nyimbo zotamanda dzina lanu, inu Wamʼmwambamwamba.+

ב [Beth]

 3 Adani anga akathawa,+

Adzapunthwa nʼkuwonongedwa pamaso panu.

 4 Chifukwa mumanditeteza kuti mlandu wanga uweruzidwe mwachilungamo.

Mwakhala pampando wanu wachifumu ndipo mukuweruza mwachilungamo.+

ג [Gimel]

 5 Mwadzudzula mitundu ya anthu+ ndipo mwawononga anthu oipa,

Nʼkufufuta dzina lawo kwamuyaya.

 6 Mdani wawonongedwa mpaka kalekale.

Mwawononganso mizinda yawo,

Ndipo sadzakumbukiridwanso.+

ה [He]

 7 Koma Yehova ndi mfumu mpaka kalekale.+

Iye akupitiriza kulamulira ndipo nthawi zonse amaweruza mwachilungamo.+

 8 Iye adzaweruza anthu okhala padziko lapansi mwachilungamo.+

Adzapereka zigamulo zolungama pa milandu ya mitundu ya anthu.+

ו [Waw]

 9 Yehova adzakhala malo otetezeka* komwe anthu oponderezedwa angathawireko,+

Malo otetezeka othawirako pa nthawi ya mavuto.+

10 Anthu odziwa dzina lanu adzakukhulupirirani.+

Simudzasiya anthu amene amakufunafunani, inu Yehova.+

ז [Zayin]

11 Imbani nyimbo zotamanda Yehova, amene akukhala mu Ziyoni.

Dziwitsani mitundu ya anthu za ntchito zake.+

12 Mulungu adzakumbukira anthu ovutika ndipo adzabwezera anthu amene anawapha.+

Iye sadzaiwala kulira kwa anthu ovutikawo.+

ח [Heth]

13 Ndikomereni mtima inu Yehova. Inu amene mukundichotsa pakhomo la imfa,+

Onani mmene anthu amene akudana nane akundizunzira,

14 Kuti ndilengeze ntchito zanu zotamandika pamageti a mwana wamkazi wa Ziyoni,*+

Komanso kuti ndisangalale chifukwa mwandipulumutsa.+

ט [Teth]

15 Mitundu ya anthu yagwera mʼdzenje limene anakumba okha.

Phazi lawo lakodwa mu ukonde umene anatchera okha.+

16 Yehova amadziwika ndi ziweruzo zimene amapereka.+

Woipa wakodwa mumsampha umene watchera yekha.+

Higayoni.* (Selah)

י [Yod]

17 Anthu oipa adzapita ku Manda,*

Anthu a mitundu yonse amene aiwala Mulungu adzapita kumeneko.

18 Koma Mulungu sadzaiwala anthu osauka,+

Ndiponso chiyembekezo cha anthu ofatsa sichidzatha.+

כ [Kaph]

19 Nyamukani, inu Yehova! Musalole kuti munthu apambane.

Mitundu ya anthu iweruzidwe pamaso panu.+

20 Achititseni mantha, inu Yehova,+

Chititsani kuti mitundu ya anthu idziwe kuti iwo ndi anthu basi. (Selah)

ל [Lamed]

10 Nʼchifukwa chiyani inu Yehova mukuima kutali?

Nʼchifukwa chiyani mukubisala pa nthawi ya mavuto?+

 2 Modzikuza, munthu woipa amathamangitsa munthu wovutika,+

Koma adzakodwa mumsampha wa ziwembu zake.+

 3 Chifukwa munthu woipa amanena za zolinga zake* zadyera modzitamandira,+

Ndipo amadalitsa munthu wadyera.

נ [Nun]

Iye amanyoza Yehova.

 4 Chifukwa cha kudzikweza, munthu woipa safufuza kuti adziwe Mulungu.

Iye amangoganiza kuti: “Kulibe Mulungu.”+

 5 Zochita zake zikupitiriza kumuyendera bwino,+

Koma zigamulo zanu sangathe kuzimvetsa.+

Iye amanyogodola adani ake onse.

 6 Mumtima mwake amanena kuti: “Sindidzagwedezeka.*

Ku mibadwomibadwo,

Tsoka silidzandigwera.”+

פ [Pe]

 7 Mʼkamwa mwake mwadzaza matemberero, mabodza ndi kuopseza ena.+

Pansi pa lilime lake pali mavuto ndi zopweteka ena.+

 8 Iye amabisalira anthu pafupi ndi midzi.

Amachoka pamene wabisalapo nʼkupha munthu wosalakwa.+

ע [Ayin]

Maso ake akuyangʼanayangʼana munthu woti amuchite chiwembu.+

 9 Amadikirira anthu pamalo amene iye amabisala ngati mkango umene uli pamalo ake amene umabisala.*+

Amadikirira kuti agwire munthu wovutika.

Amagwira munthu wovutikayo pomukulunga ndi ukonde wake.+

10 Munthu wovutikayo amaponderezedwa ndipo amawerama ndi chisoni.

Anthu ovutikawo amagwidwa ndi dzanja lake lamphamvu.

11 Mumtima mwake amanena kuti: “Mulungu waiwala zoipa zimene ndimachita.+

Iye wayangʼana kumbali.

Sakuona chilichonse.”+

ק [Qoph]

12 Nyamukani, inu Yehova.+ Inu Mulungu, chitanipo kanthu.+

Musaiwale anthu ovutika.+

13 Nʼchifukwa chiyani munthu woipa wanyoza Mulungu?

Mumtima mwake amanena kuti: “Simudzandiimba mlandu.”

ר [Resh]

14 Koma inu mumaona mavuto ndi masautso.

Mumayangʼana nʼkuchitapo kanthu.+

Munthu wovutika amayangʼana kwa inu,+

Mumathandiza mwana wamasiye.+

ש [Shin]

15 Thyolani dzanja la munthu woipa ndi wankhanza,+

Kuti mukamafufuza zoipa zake

Musazipezenso.

16 Yehova ndi Mfumu mpaka kalekale.+

Mitundu ya anthu yawonongedwa, yachotsedwa padziko lapansi.+

ת [Taw]

17 Koma inu Yehova mudzamva pempho la anthu ofatsa.+

Mudzalimbitsa mitima yawo+ ndipo mudzawamvetsera mwatcheru.+

18 Mudzaweruza mwachilungamo mwana wamasiye komanso anthu oponderezedwa,+

Kuti munthu wamba wochokera kufumbi asadzawachititsenso mantha.+

Kwa wotsogolera nyimbo. Salimo la Davide.

11 Ine ndathawira kwa Yehova.+

Ndiye nʼchifukwa chiyani mukundiuza kuti:

“Thawira kuphiri ngati mbalame!

 2 Onani mmene anthu oipa akungira uta,

Aika mivi yawo pa chingwe cha uta,

Kuti alase anthu owongoka mtima kuchokera pamalo amdima.

 3 Kodi munthu wolungama angachite chiyani

Maziko achilungamo atagumulidwa?”

 4 Yehova ali mʼkachisi wake wopatulika.+

Mpando wachifumu wa Yehova uli kumwamba.+

Maso ake amaona, inde maso ake* amayangʼanitsitsa ana a anthu.+

 5 Yehova amayangʼanitsitsa munthu wolungama komanso munthu woipa.+

Mulungu amadana ndi aliyense amene amakonda chiwawa.+

 6 Oipa, iye adzawagwetsera misampha* ngati mvula.

Moto ndi sulufule+ komanso mphepo yotentha zidzakhala chakumwa chawo.

 7 Chifukwa Yehova ndi wolungama.+ Iye amakonda ntchito zolungama.+

Anthu owongoka mtima adzaona nkhope yake.*+

Kwa wotsogolera nyimbo. Aimbe nyimboyi pa Sheminiti.* Nyimbo ya Davide.

12 Ndipulumutseni, inu Yehova, chifukwa anthu okhulupirika atha.

Anthu okhulupirika atheratu pakati pa anthu.

 2 Iwo amauzana zinthu zabodza.

Ndi milomo yawo, amayamikira ena mwachiphamaso* komanso kulankhula ndi mtima wachinyengo.*+

 3 Yehova adzadula milomo yonse yolankhula zachinyengo

Komanso lilime lolankhula modzikweza.+

 4 Iye adzadula anthu amene amanena kuti: “Ndi lilime lathu tidzapambana.

Timagwiritsa ntchito milomo yathu mmene tikufunira.

Ndi ndani angatilamulire?”+

 5 Yehova wanena kuti: “Chifukwa chakuti ovutika akuponderezedwa

Chifukwa cha kuusa moyo kwa anthu osauka,+

Ndidzanyamuka nʼkuchitapo kanthu,

Ndidzawapulumutsa kwa anthu amene akuwanyoza.”*

 6 Mawu a Yehova ndi oyera.+

Ali ngati siliva woyengedwa mungʼanjo yadothi nthawi zokwanira 7.

 7 Inu Yehova mudzawayangʼanira.+

Aliyense wa iwo mudzamuteteza ku mʼbadwo uwu mpaka kalekale.

 8 Anthu oipa akungoyendayenda popanda wowaletsa,

Chifukwa chakuti ana a anthu amalimbikitsa anthu kuchita zinthu zoipa.+

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ya Davide.

13 Kodi mudzandiiwala mpaka liti, inu Yehova? Mpaka kalekale?

Kodi mudzandibisira nkhope yanu mpaka liti?+

 2 Kodi ndidzapitiriza kuvutika ndi nkhawa,

Komanso tsiku lililonse ndidzakhala ndi chisoni mumtima mwanga mpaka liti?

Kodi mdani wanga adzapambana mpaka liti?+

 3 Ndiyangʼaneni ndipo mundiyankhe, inu Yehova Mulungu wanga.

Chititsani maso anga kuti aone kuwala, kuti ndisagone mu imfa.

 4 Chitani zimenezi kuti mdani wanga asanene kuti: “Ndamugonjetsa!”

Musalole kuti adani anga asangalale chifukwa chakuti ndagwa.+

 5 Koma ine ndakhulupirira chikondi chanu chokhulupirika+

Mtima wanga udzasangalala chifukwa cha chipulumutso chanu.+

 6 Ndidzaimbira Yehova chifukwa wandipatsa mphoto yaikulu.+

Kwa wotsogolera nyimbo. Salimo la Davide.

14 Munthu wopusa* amanena mumtima mwake kuti:

“Kulibe Yehova.”+

Zochita za anthu amenewa ndi zoipa komanso zonyansa,

Ndipo palibe amene akuchita zabwino.+

 2 Koma kuchokera kumwamba, Yehova amayangʼana ana a anthu,

Kuti aone ngati pali aliyense wozindikira, ngati pali aliyense amene akufunafuna Yehova.+

 3 Onse apatuka,+

Ndipo onsewo ndi achinyengo.

Palibe aliyense amene akuchita zabwino,

Palibiretu ndi mmodzi yemwe.

 4 Kodi palibe aliyense womvetsa zinthu pakati pa anthu ochita zoipawa?

Iwo amadya anthu anga ngati kuti akudya chakudya.

Ndipo sapemphera kwa Yehova.

 5 Koma adzagwidwa ndi mantha aakulu,+

Chifukwa Yehova ali pakati pa mʼbadwo wa anthu olungama.

 6 Inu anthu ochita zoipa mumayesetsa kusokoneza mapulani a munthu wonyozeka,

Koma Yehova ndi malo ake othawirako.+

 7 Zikanakhala bwino chipulumutso cha Isiraeli chikanachokera ku Ziyoni.+

Yehova akadzabwezeretsa anthu ake amene anagwidwa nʼkutengedwa kupita kudziko lina,

Yakobo adzasangalale, Isiraeli adzakondwere.

Nyimbo ya Davide.

15 Inu Yehova, ndi ndani amene angakhale mlendo mutenti yanu?

Ndi ndani amene angakhale mʼphiri lanu lopatulika?+

 2 Ndi amene akuyenda mosalakwitsa zinthu,*+

Amene amachita zinthu zabwino+

Komanso kulankhula zoona mumtima mwake.+

 3 Iye sanena miseche ndi lilime lake,+

Sachitira mnzake choipa chilichonse,+

Ndipo sanyoza* anzake.+

 4 Iye sagwirizana ndi munthu aliyense wonyansa,+

Koma amalemekeza anthu amene amaopa Yehova.

Sasintha zimene walonjeza* ngakhale zinthu zitakhala kuti sizili bwino kwa iye.+

 5 Sakongoza ndalama zake kuti alandire chiwongoladzanja,+

Ndipo salandira chiphuphu kuti akhotetse mlandu wa munthu wosalakwa.+

Munthu aliyense amene amachita zimenezi, sadzagwedezeka.*+

Mikitamu* ya Davide.

16 Nditetezeni, inu Mulungu, chifukwa ndathawira kwa inu.+

 2 Ndauza Yehova kuti: “Inu ndinu Yehova. Zinthu zonse zabwino pa moyo wanga zimachokera kwa inu.*

 3 Ndipo oyera amene ali padziko lapansi,

Anthu aulemerero amenewo, ndi amene amandichititsa kukhala wosangalala kwambiri.”+

 4 Anthu amene amafunitsitsa kulambira milungu ina amachulukitsa chisoni chawo.+

Ine sindidzapereka nsembe zachakumwa za magazi kwa milungu ina,

Ndipo milomo yanga sidzatchula mayina awo.+

 5 Yehova ndi gawo langa, gawo limene ndinapatsidwa+ komanso kapu yanga.+

Inu mumateteza cholowa changa.

 6 Malo amene andiyezera ndi abwino kwambiri.

Inde, ndikukhutira ndi cholowa chimene ndapatsidwa.+

 7 Ndidzatamanda Yehova amene wandipatsa malangizo.+

Ngakhale usiku maganizo amkati mwa mtima wanga* amandiuza zoyenera kuchita.+

 8 Ndimaika Yehova patsogolo panga nthawi zonse.+

Chifukwa iye ali kudzanja langa lamanja, sindidzagwedezeka.*+

 9 Choncho mtima wanga ukusangalala, ndikusangalala kwambiri.*

Ndipo ndikukhala motetezeka.

10 Chifukwa simudzandisiya* mʼManda.*+

Simudzalola kuti wokhulupirika wanu aone dzenje.*+

11 Mumandidziwitsa njira ya moyo.+

Ndikakhala nanu pafupi,* ndimasangalala kwambiri.+

Kudzanja lanu lamanja kuli chimwemwe* mpaka kalekale.

Pemphero la Davide.

17 Imvani dandaulo langa lopempha kuti mundichitire chilungamo, inu Yehova.

Mvetserani kulira kwanga kopempha thandizo.

Imvani pemphero langa lopanda chinyengo.+

 2 Mupereke chigamulo chachilungamo mʼmalo mwa ine.+

Maso anu aone kuti ndine wolungama.

 3 Mwafufuza mtima wanga, mwandifufuza ngakhale usiku,+

Ndipo mwandiyenga.+

Mudzapeza kuti ndinalibe zolinga zochita choipa chilichonse.

Ndipo pakamwa panga sipanachimwe.

 4 Kunena za ntchito za anthu,

Mogwirizana ndi mawu apakamwa panu, ndapewa kuyenda mʼnjira za wachifwamba.+

 5 Ndithandizeni kuti ndipitirize kuyenda mʼnjira zanu,

Kuti mapazi anga asapunthwe.+

 6 Ine ndikuitana inu, chifukwa mudzandiyankha,+ inu Mulungu.

Tcherani khutu* kwa ine. Imvani mawu anga.+

 7 Sonyezani modabwitsa chikondi chanu chokhulupirika,+

Inu Mpulumutsi wa anthu amene amathawira kudzanja lanu lamanja

Kuthawa anthu amene akupandukirani.

 8 Nditetezeni ngati mwana wa diso lanu,+

Ndibiseni mumthunzi wa mapiko anu.+

 9 Nditetezeni kwa anthu oipa amene akundiukira,

Kwa adani* ochokera kufumbi amene andizungulira.+

10 Mitima yawo siimva chisoni,*

Ndipo amalankhula modzikuza ndi pakamwa pawo.

11 Tsopano adaniwo atizungulira,+

Akufufuza mpata kuti atigwetse.*

12 Ali ngati mkango umene ukufunitsitsa kukhadzula nyama,

Ngati mkango wamphamvu umene wabisalira nyama.

13 Nyamukani, inu Yehova, mulimbane naye+ nʼkumugwetsa.

Ndipulumutseni kwa woipayo ndi lupanga lanu.

14 Ndipulumutseni ndi dzanja lanu, inu Yehova,

Kwa anthu amʼdzikoli* amene gawo lawo lili mʼmoyo uno,+

Anthu amene mwawakhutitsa ndi zinthu zabwino zimene mumapereka+

Omwe amasiyira cholowa ana awo aamuna ochuluka.

15 Koma ine ndidzaona nkhope yanu mʼchilungamo.

Ndikadzuka ndimadziwa kuti muli nane* ndipo ndimakhutira.+

Kwa wotsogolera nyimbo. Salimo la mtumiki wa Yehova, Davide, amene anauza Yehova mawu amʼnyimbo iyi pa tsiku limene Yehova anamulanditsa mʼmanja mwa adani ake onse komanso mʼmanja mwa Sauli. Iye anati:+

18 Ndimakukondani inu Yehova, mphamvu yanga.+

 2 Yehova ndi thanthwe langa, malo anga achitetezo ndiponso amene amandipulumutsa.+

Mulungu wanga ndi thanthwe langa+ limene ndimathawirako,

Iye ndi chishango changa, nyanga* yanga ya chipulumutso* komanso malo anga othawirako otetezeka.*+

 3 Ndidzaitana Yehova, amene ndi woyenera kutamandidwa,

Ndipo adzandipulumutsa kwa adani anga.+

 4 Zingwe za imfa zinandikulunga,+

Gulu la anthu opanda pake, amene anali ngati madzi osefukira, ankandiopseza.+

 5 Zingwe za Manda* zinandizungulira.

Ananditchera misampha ya imfa.+

 6 Pa nthawi ya mavuto anga ndinaitana Yehova,

Ndinapitiriza kufuulira Mulungu wanga kuti andithandize.

Iye anamva mawu anga ali mʼkachisi wake,+

Ndipo makutu ake anamva kulira kwanga kopempha thandizo.+

 7 Kenako dziko lapansi linayamba kugwedezeka ndi kunjenjemera.+

Maziko a mapiri ananjenjemera,

Komanso anagwedezeka chifukwa Mulungu anakwiya.+

 8 Utsi unatuluka mʼmphuno mwake,

Ndipo moto wowononga unatuluka mʼkamwa mwake.+

Makala oyaka anatuluka mwa iye.

 9 Iye anaweramitsa kumwamba pamene ankatsika,+

Ndipo mdima wandiweyani unali pansi pa mapazi ake.+

10 Iye anakwera pakerubi ndipo anabwera akuuluka.+

Mulungu anauluka mwaliwiro pamapiko a mngelo.*+

11 Kenako anadziphimba ndi mdima,+

Panali madzi akuda ndi mtambo wakuda+

Zimene zinamuzungulira ngati tenti yake.

12 Kuwala kunangʼanima pamaso pake,

Ndipo matalala ndi makala a moto anatuluka mʼmitambo.

13 Kenako Yehova anayamba kugunda ngati mabingu ali kumwamba.+

Wamʼmwambamwamba anachititsa kuti mawu ake amveke,+

Ndipo kunagwa matalala ndi makala a moto.

14 Anaponya mivi yake nʼkuwabalalitsa.+

Anaponya mphezi zake nʼkuwachititsa kuti asokonezeke.+

15 Pansi pa mitsinje* panayamba kuonekera.+

Maziko a dziko lapansi anayamba kuonekera chifukwa cha kudzudzula kwanu, inu Yehova,

Komanso chifukwa cha mphamvu ya mpweya wotuluka mʼmphuno mwanu.+

16 Anatambasula dzanja lake kuchokera kumwamba,

Anandigwira nʼkundivuula mʼmadzi akuya.+

17 Anandipulumutsa kwa mdani wanga wamphamvu,+

Kwa anthu odana nane amene anali amphamvu kuposa ine.+

18 Adaniwo anandiukira pa tsiku la tsoka langa,+

Koma Yehova anandithandiza.

19 Ananditenga nʼkundiika pamalo otetezeka.*

Anandipulumutsa chifukwa ankasangalala nane.+

20 Yehova amandidalitsa mogwirizana ndi chilungamo changa.+

Amandipatsa mphoto chifukwa choti ndine wosalakwa.*+

21 Ndasunga njira za Yehova,

Ndipo sindinachite chinthu choipa kwambiri, chomwe ndi kusiya Mulungu wanga.

22 Ndimakumbukira ziweruzo zake zonse,

Ndipo sindidzanyalanyaza malamulo ake.

23 Ndidzakhalabe wosalakwa pamaso pake,+

Ndipo ndidzayesetsa kupewa cholakwa.+

24 Yehova andipatse mphoto chifukwa choti ndine wolungama,+

Komanso chifukwa choti ndine wosalakwa pamaso pake.+

25 Munthu wokhulupirika, mumamuchitira zinthu mokhulupirika.+

Munthu wopanda cholakwa, mumamuchitira zinthu mwachilungamo.+

26 Kwa munthu woyera, mumasonyeza kuti ndinu woyera,+

Koma kwa munthu wopotoka maganizo mumasonyeza kuti ndinu wochenjera.+

27 Inu mumapulumutsa anthu onyozeka,*+

Koma anthu odzikweza* mumawatsitsa.+

28 Chifukwa inuyo Yehova ndi amene mumayatsa nyale yanga,

Mulungu wanga amandiunikira mumdima.+

29 Ndi thandizo lanu, ndingalimbane ndi gulu la achifwamba.+

Ndi mphamvu za Mulungu ndingakwere khoma.+

30 Njira ya Mulungu woona ndi yangwiro.+

Mawu a Yehova ndi oyengeka bwino.+

Iye ndi chishango kwa anthu onse amene amathawira kwa iye.+

31 Kodi pali Mulungu winanso woposa Yehova?+

Nanga pali thanthwe linanso kupatula Mulungu wathu?+

32 Mulungu woona ndi amene amandipatsa mphamvu,+

Ndipo adzasalaza njira yanga.+

33 Iye amachititsa mapazi anga kuti akhale ngati a mbawala,

Amachititsa kuti ndiime pamalo okwera.+

34 Iye amaphunzitsa manja anga kumenya nkhondo,

Manja anga angathe kukunga uta wakopa.*

35 Inu mumandipatsa chishango chanu chachipulumutso,+

Dzanja lanu lamanja limandithandiza,*

Ndipo kudzichepetsa kwanu nʼkumene kumandikweza.+

36 Mumakulitsa njira kuti mapazi anga azidutsamo,

Ndipo mapazi anga sadzaterereka.+

37 Ndidzathamangitsa adani anga nʼkuwapeza,

Sindidzabwerera mpaka onse nditawawononga.

38 Ndidzawaphwanya kuti asadzukenso.+

Ndidzawapondaponda ndi mapazi anga.

39 Inu mudzandipatsa mphamvu kuti ndithe kumenya nkhondo.

Mudzachititsa kuti adani anga agonje.+

40 Mudzachititsa kuti adani anga athawe pamaso panga,*

Ndipo ndidzapha* anthu amene amadana nane.+

41 Iwo amafuula kuti athandizidwe, koma palibe amene angawapulumutse,

Amafika pofuulira Yehova, koma iye samawayankha.

42 Ndidzawapera ndipo adzakhala ngati fumbi louluzika ndi mphepo.

Ndidzawakhuthula ngati matope mumsewu.

43 Inu mudzandipulumutsa kwa anthu a mtundu wanga ondipezera zifukwa.+

Mudzandiika kuti ndikhale mtsogoleri wa mitundu ya anthu.+

Anthu amene sindikuwadziwa adzanditumikira.+

44 Anthu akadzangomva mphekesera zokhudza ine, adzandimvera.

Anthu ochokera mʼdziko lina adzandigwadira mwamantha.+

45 Anthu ochokera mʼdziko lina adzachita mantha,*

Iwo adzatuluka mʼmalo awo otetezeka akunjenjemera.

46 Yehova ndi wamoyo. Litamandike Thanthwe langa.+

Mulungu amene amandipulumutsa alemekezeke.+

47 Mulungu woona amabwezera adani anga.+

Iye amachititsa kuti mitundu ya anthu izindigonjera.

48 Iye amandipulumutsa kwa adani anga olusa.

Mumandikweza pamwamba pa anthu amene amandiukira.+

Mumandipulumutsa kwa munthu wachiwawa.

49 Nʼchifukwa chake ndidzakulemekezani, inu Yehova, pakati pa mitundu ya anthu.+

Ndipo ndidzaimba nyimbo zotamanda dzina lanu.+

50 Iye amachita zazikulu kuti apulumutse mfumu yake,+

Amasonyeza chikondi chokhulupirika kwa wodzozedwa wake,+

Kwa Davide ndi mbadwa* zake mpaka kalekale.+

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ya Davide.

19 Zinthu zakumwamba zikulengeza ulemerero wa Mulungu.+

Ndipo mumlengalenga mukufotokoza ntchito ya manja ake.+

 2 Tsiku lililonse, mawu awo amamveka,

Ndipo usiku uliwonse zimasonyeza nzeru zake.

 3 Sizilankhula kapena kutulutsa mawu.

Mawu awo samveka.

 4 Koma mawu awo amveka* padziko lonse lapansi,

Ndipo uthenga wawo wamveka kumalekezero a dziko lapansi kumene kuli anthu.+

Mulungu wamangira dzuwa tenti kumwamba.

 5 Dzuwalo limaoneka ngati mkwati amene akutuluka mʼchipinda chake,

Limasangalala ngati mwamuna wamphamvu amene akuthamanga pampikisano.

 6 Limatuluka kuchokera kumalekezero ena akumwamba,

Nʼkuzungulira mpaka kumalekezero enanso.+

Ndipo palibe chilichonse chimene sichimva kutentha kwake.

 7 Chilamulo cha Yehova ndi changwiro,+ chimabwezeretsa mphamvu.*+

Zikumbutso za Yehova ndi zodalirika,+ zimapatsa nzeru munthu wosadziwa zinthu.+

 8 Malamulo ochokera kwa Yehova ndi olungama, amasangalatsa mtima.+

Chilamulo cha Yehova ndi choyera, chimatsegula maso.+

 9 Kuopa Yehova+ nʼkoyera, ndipo kudzakhalapo kwamuyaya.

Zigamulo za Yehova nʼzolondola, ndipo pa mbali iliyonse ndi zolungama.+

10 Nʼzosilirika kuposa golide,

Kuposa golide wambiri woyengeka bwino.+

Ndipo nʼzotsekemera kuposa uchi,+ kuposa uchi umene ukukha mʼzisa.

11 Ndiponso mtumiki wanu amachenjezedwa nazo.+

Munthu wosunga zigamulozo amapeza mphoto yaikulu.+

12 Ndi ndani amene angazindikire yekha zinthu zimene walakwitsa?+

Mundikhululukire machimo amene ndachita mosadziwa.

13 Ndipo mundiletse kuchita zinthu modzikuza, ine mtumiki wanu.+

Musalole kuti kudzikuza kundilamulire.+

Mukatero ndidzakhala wopanda chifukwa,+

Komanso ndidzakhala wopanda mlandu wa machimo akuluakulu.*

14 Mawu apakamwa panga komanso zimene ndimaganizira mozama mumtima mwanga,

Zizikusangalatsani, inu Yehova,+ Thanthwe langa+ ndiponso Wondiwombola.+

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ya Davide.

20 Yehova akuyankheni pa tsiku la mavuto.

Dzina la Mulungu wa Yakobo likutetezeni.+

 2 Akutumizireni thandizo kuchokera kumalo ake opatulika+

Ndipo akuthandizeni ali ku Ziyoni.+

 3 Akumbukire nsembe zanu zonse zimene munapereka monga mphatso.

Alandire mosangalala* nsembe zanu zopsereza. (Selah)

 4 Akupatseni zimene mtima wanu umalakalaka+

Ndipo achititse kuti mapulani anu onse ayende bwino.*

 5 Tidzafuula mosangalala chifukwa cha mmene mwatipulumutsira,+

Tidzakweza mbendera zathu mʼdzina la Mulungu wathu.+

Yehova akwaniritse zopempha zanu zonse.

 6 Tsopano ndadziwa kuti Yehova amapulumutsa wodzozedwa wake.+

Amamuyankha kuchokera kumwamba kwake koyera,

Pomupulumutsa modabwitsa ndi dzanja lake lamanja.+

 7 Ena amadalira magaleta ndipo ena amadalira mahatchi,+

Koma ife timadalira dzina la Yehova Mulungu wathu.+

 8 Anthu amenewo akomoka ndipo agwa,

Koma ife tadzuka ndipo taimirira.+

 9 Inu Yehova, pulumutsani mfumu!+

Tsiku limene tidzapemphe kuti atithandize, Mulungu adzatiyankha.+

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ya Davide.

21 Inu Yehova, mfumu ikusangalala chifukwa mwasonyeza kuti ndinu wamphamvu.+

Ikusangalala kwambiri chifukwa mwaipulumutsa.+

 2 Mwaipatsa zimene mtima wake umalakalaka,+

Ndipo simunaimane zopempha za milomo yake. (Selah)

 3 Mumaipatsa madalitso ambiri,

Ndipo munaiveka chisoti chachifumu chagolide woyenga bwino.+

 4 Mfumuyo inakupemphani moyo wautali ndipo munaipatsadi.+

Munaipatsa moyo wautali* kuti ikhale mpaka kalekale.

 5 Ulemerero wake ndi waukulu chifukwa mwaipulumutsa.+

Mwaipatsa ulemu ndi ulemerero.

 6 Mwaipatsa madalitso mpaka kalekale.+

Mwaichititsa kuti ikhale yosangalala chifukwa muli nayo pafupi.*+

 7 Mfumu imakhulupirira Yehova.+

Chifukwa cha chikondi chokhulupirika cha Wamʼmwambamwamba, mfumuyo sidzagwedezeka.*+

 8 Dzanja lanu lidzapeza adani anu onse.

Dzanja lanu lamanja lidzapeza anthu amene amadana nanu.

 9 Mudzawawononga ngati kuti mwawaponya mungʼanjo yamoto, pa nthawi imene mudzaonekere.

Yehova adzawameza atakwiya ndipo moto udzawapsereza.+

10 Ana awo mudzawawononga kuwachotsa padziko lapansi,

Ndipo mbadwa zawo mudzazichotsa pakati pa ana a anthu.

11 Chifukwa akonza zoti akuchitireni zoipa.+

Akonza ziwembu zimene zidzalephereka.+

12 Inu mudzawachititsa kuti athawe.+

Mudzachita zimenezi powalozetsa* muvi wa uta wanu.

13 Nyamukani, inu Yehova, muonetse mphamvu zanu.

Tidzaimba nyimbo zotamanda mphamvu zanu.

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimboyi iimbidwe motsatira “Mbawala Yaikazi ya Mʼbandakucha.”* Nyimbo ya Davide.

22 Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyiranji ine?+

Nʼchifukwa chiyani mukuchedwa kundipulumutsa?

Nʼchifukwa chiyani simukumva kubuula kwanga?+

 2 Inu Mulungu wanga, ine ndimakuitanani masana, koma simundiyankha.+

Ndipo usiku sindikhala chete, ndimaitanabe.

 3 Koma inu ndinu woyera,+

Ndipo mwazunguliridwa ndi* mawu otamanda a Isiraeli.

 4 Makolo athu ankadalira inu.+

Iwo ankakudalirani ndipo inu munkawapulumutsa.+

 5 Iwo ankafuulira inu ndipo munkawapulumutsa.

Ankakudalirani ndipo simunawakhumudwitse.*+

 6 Koma ine ndine nyongolotsi osati munthu,

Anthu amandinyogodola* komanso kundinyoza.+

 7 Anthu onse amene amandiona amandiseka.+

Iwo amandinyogodola nʼkumapukusa mitu yawo mondinyoza nʼkumati:+

 8 “Anadzipereka kwa Yehova. Tiyeni tione ngati angamupulumutse!

Musiyeni Mulungu amupulumutse, chifukwa amamukonda kwambiri!”+

 9 Inu ndi amene munanditulutsa mʼmimba,+

Ndinu amene munandichititsa kumva kuti ndine wotetezeka pamene ndinkayamwa mabere a mayi anga.

10 Ndinaperekedwa kwa inu kuti muzindisamalira* kuyambira pamene ndinabadwa.

Kuyambira ndili mʼmimba mwa mayi anga, inu mwakhala Mulungu wanga.

11 Musakhale kutali ndi ine, chifukwa mavuto ali pafupi+

Ndipo palibe winanso amene angandithandize.+

12 Ngʼombe zazingʼono zamphongo zochuluka zandizungulira.+

Ngʼombe zamphongo zamphamvu za ku Basana zandizungulira.+

13 Iwo atsegula pakamwa pawo nʼkumandiopseza,+

Ngati mkango wobangula umene umakhadzulakhadzula nyama.+

14 Ndathiridwa pansi ngati madzi.

Mafupa anga onse aguluka.

Mtima wanga wakhala ngati phula,+

Ukusungunuka mkati mwanga.+

15 Mphamvu zanga zauma ngati phale.+

Lilime langa lamatirira kunkhama zanga,+

Ndipo mwandilowetsa mʼdzenje kuti ndife.+

16 Adani anga andizungulira ngati agalu.+

Andizungulira ngati gulu la anthu ochita zoipa,+

Mofanana ndi mkango, iwo akundiluma manja ndi mapazi.+

17 Ndingathe kuwerenga mafupa anga onse.+

Adaniwo akuona zimenezi ndipo akundiyangʼanitsitsa.

18 Iwo akugawana zovala zanga,

Ndipo akuchita maere pa zovala zanga.+

19 Koma inu Yehova, musakhale kutali ndi ine.+

Inu ndinu mphamvu zanga, ndithandizeni mofulumira.+

20 Ndipulumutseni ku lupanga,

Pulumutsani moyo wanga wamtengo wapatali* mʼkamwa* mwa agalu.+

21 Ndipulumutseni mʼkamwa mwa mkango+ komanso kunyanga za ngʼombe zamphongo zamʼtchire.

Mundiyankhe ndi kundipulumutsa.

22 Ndidzalengeza dzina lanu kwa abale anga.+

Ndidzakutamandani pakati pa mpingo.+

23 Inu amene mumaopa Yehova, mutamandeni!

Inu nonse mbadwa* za Yakobo, mʼpatseni ulemerero!+

Muopeni, inu nonse mbadwa* za Isiraeli.

24 Chifukwa iye sananyoze kapena kunyansidwa ndi kuvutika kwa munthu woponderezedwa.+

Sanabise nkhope yake kwa iye.+

Pamene anamulirira kuti amuthandize, iye anamva.+

25 Ndidzakutamandani mumpingo waukulu.+

Ndidzakwaniritsa malonjezo anga pamaso pa anthu amene amamuopa.

26 Ofatsa adzadya nʼkukhuta.+

Anthu amene akufunafuna Yehova adzamutamanda.+

Musangalale ndi moyo* mpaka kalekale.

27 Anthu onse ochokera kumalekezero a dziko lapansi adzakumbukira Yehova nʼkupita kwa iye.

Ndipo mabanja onse a mitundu ya anthu adzagwada pamaso panu.+

28 Chifukwa Yehova ndi Mfumu,+

Ndipo akulamulira mitundu ya anthu.

29 Anthu onse olemera* padziko lapansi adzadya ndipo adzamuweramira.

Anthu onse amene amabwerera kufumbi adzagwada pamaso pake,

Ndipo palibe aliyense wa iwo amene angapulumutse moyo wawo.

30 Mbadwa* zawo zidzamutumikira.

Mibadwo yamʼtsogolo idzauzidwa zokhudza Yehova.

31 Adzabwera nʼkunena za chilungamo chake.

Adzauza anthu amene adzabadwe zimene iye wachita.

Nyimbo ya Davide.

23 Yehova ndi Mʼbusa wanga.+

Sindidzasowa kanthu.+

 2 Amandigoneka mʼmalo odyetsera ziweto a msipu wambiri.

Amanditsogolera kumalo opumira a madzi ambiri.*+

 3 Amanditsitsimula.*+

Amanditsogolera munjira zachilungamo chifukwa cha dzina lake.+

 4 Ngakhale ndikuyenda mʼchigwa chamdima wandiweyani,+

Sindikuopa kanthu,+

Chifukwa inu muli ndi ine.+

Chibonga chanu ndi ndodo yanu zikundipangitsa kumva kuti ndine wotetezeka.*

 5 Mumandipatsa chakudya patebulo pamaso pa adani anga.+

Ndimatsitsimulidwa mukandidzoza mafuta kumutu.+

Kapu yanga ndi yodzaza bwino.+

 6 Ndithu, masiku onse a moyo wanga ndidzasangalala ndi ubwino wanu komanso chikondi chanu chokhulupirika,+

Ndipo ndidzakhala mʼnyumba ya Yehova kwa moyo wanga wonse.+

Salimo la Davide. Nyimbo.

24 Dziko lapansi ndiponso zonse zimene zili mmenemo ndi za Yehova,+

Nthaka komanso onse okhala panthakapo ndi ake.

 2 Iye anakhazika dziko lapansi molimba panyanja+

Ndipo analikhazikitsa mwamphamvu pamitsinje.

 3 Ndi ndani angakwere kuphiri la Yehova,+

Ndipo ndi ndani angaime mʼmalo ake opatulika?

 4 Aliyense amene ndi wosalakwa komanso wopanda chinyengo mumtima mwake,+

Amene sanalumbire mwachinyengo potchula moyo Wanga,*

Kapena kulumbira pofuna kupusitsa anthu ena.+

 5 Iye adzalandira madalitso kuchokera kwa Yehova,+

Komanso chilungamo kuchokera kwa Mulungu amene amamupulumutsa.+

 6 Umenewu ndi mʼbadwo wa anthu amene amafunafuna Mulungu,

Mʼbadwo wa anthu amene amafunafuna nkhope yanu, inu Mulungu wa Yakobo. (Selah)

 7 Tukulani mitu yanu, inu mageti,+

Tsegukani,* inu makomo akale,

Kuti Mfumu yaulemerero ilowe!+

 8 Kodi Mfumu yaulemerero imeneyi ndi ndani?

Ndi Yehova, wanyonga ndi wamphamvu,+

Yehova, wamphamvu pankhondo.+

 9 Tukulani mitu yanu, inu mageti,+

Tsegukani, inu makomo akale,

Kuti Mfumu yaulemerero ilowe!

10 Kodi Mfumu yaulemerero imeneyi ndi ndani?

Ndi Yehova wa magulu ankhondo akumwamba. Iye ndi Mfumu yaulemerero.+ (Selah)

Salimo la Davide.

א [Aleph]

25 Ndapereka moyo wanga kwa inu Yehova.

ב [Beth]

 2 Inu Mulungu wanga, ndimakudalirani.+

Musalole kuti ndichite manyazi.+

Musalole kuti adani anga asangalale chifukwa cha mavuto anga.+

ג [Gimel]

 3 Ndithudi, palibe anthu amene amayembekezera inu amene adzachite manyazi.+

Koma amene adzachite manyazi ndi anthu amene amachita zachinyengo popanda chifukwa.+

ד [Daleth]

 4 Ndidziwitseni njira zanu, inu Yehova.+

Ndiphunzitseni kuyenda mʼnjira zanu.+

ה [He]

 5 Ndithandizeni kuti ndiziyenda mʼchoonadi chanu ndipo mundiphunzitse,+

Chifukwa inu ndinu Mulungu amene mumandipulumutsa.

ו [Waw]

Ndimayembekezera inu tsiku lonse.

ז [Zayin]

 6 Kumbukirani chifundo chanu, inu Yehova, komanso chikondi chanu chokhulupirika,+

Zimene mumasonyeza nthawi zonse.*+

ח [Heth]

 7 Musakumbukire machimo amene ndinachita ndili mnyamata komanso zolakwa zanga.

Mundikumbukire chifukwa cha ubwino wanu, inu Yehova,+

Mogwirizana ndi chikondi chanu chokhulupirika.+

ט [Teth]

 8 Yehova ndi wabwino komanso wolungama.+

Nʼchifukwa chake amalangiza ochimwa kuti ayende mʼnjira yoyenera.+

י [Yod]

 9 Adzatsogolera ofatsa kuti azichita zinthu zoyenera,+

Ndipo adzaphunzitsa ofatsa kuti aziyenda mʼnjira yake.+

כ [Kaph]

10 Njira zonse za Yehova ndi zokhulupirika ndipo nʼzogwirizana ndi chikondi chake chokhulupirika

Kwa anthu amene amasunga pangano lake+ ndi zikumbutso zake.+

ל [Lamed]

11 Chifukwa cha dzina lanu, inu Yehova,+

Mundikhululukire tchimo langa, ngakhale kuti ndi lalikulu.

מ [Mem]

12 Ngati munthu amaopa Yehova,+

Iye adzamulangiza njira imene akuyenera kusankha.+

נ [Nun]

13 Moyo wake udzasangalala ndi zinthu zabwino,+

Ndipo mbadwa* zake zidzatenga dziko lapansi kuti likhale lawo.+

ס [Samekh]

14 Anthu amene amaopa Yehova ndi amene amakhala naye pa ubwenzi wolimba,+

Ndipo amawadziwitsa pangano lake.+

ע [Ayin]

15 Maso anga amayangʼana kwa Yehova nthawi zonse,+

Chifukwa iye ndi amene amawonjola phazi langa mu ukonde.+

פ [Pe]

16 Tembenukani nʼkundiyangʼana ndipo mundikomere mtima.

Chifukwa ndili ndekhandekha ndipo ndilibe wondithandiza.

צ [Tsade]

17 Nkhawa zamumtima mwanga zawonjezeka.+

Ndipulumutseni ku mavuto anga.

ר [Resh]

18 Onani mavuto ndi masautso anga,+

Ndipo mundikhululukire machimo anga onse.+

19 Onani mmene adani anga achulukira,

Komanso onani kuti amadana nane kwambiri.

ש [Shin]

20 Tetezani moyo wanga ndipo mundipulumutse.+

Musalole kuti ndichite manyazi, chifukwa ndathawira kwa inu.

ת [Taw]

21 Kukhala wokhulupirika komanso kuchita zinthu zoyenera kunditeteze,+

Chifukwa chiyembekezo changa chili mwa inu.+

22 Inu Mulungu, pulumutsani* Isiraeli ku mavuto ake onse.

Salimo la Davide.

26 Ndiweruzeni, inu Yehova, chifukwa ndimachita zinthu mokhulupirika.+

Nthawi zonse ndimadalira inu Yehova.+

 2 Ndifufuzeni, inu Yehova, ndipo mundiyese.

Yengani maganizo anga* komanso mtima wanga.+

 3 Chifukwa nthawi zonse ndimaganizira mozama za chikondi chanu chokhulupirika,

Ndipo ndimayenda mʼchoonadi chanu.+

 4 Sindicheza* ndi anthu achinyengo,+

Ndipo ndimapewa anthu amene amabisa umunthu wawo.*

 5 Ndimadana ndi zokhala pagulu la anthu ochita zoipa,+

Ndipo ndimakana kucheza* ndi anthu oipa.+

 6 Ndidzasamba mʼmanja mwanga kusonyeza kuti ndine wosalakwa,

Ndipo ndidzayenda mozungulira guwa lanu lansembe, inu Yehova,

 7 Kuti mawu anga oyamikira amveke,+

Komanso kuti ndilengeze ntchito zanu zonse zodabwitsa.

 8 Yehova, ndimakonda nyumba imene inu mumakhala,+

Malo amene kumakhala ulemerero wanu.+

 9 Musandiwononge limodzi ndi anthu ochimwa,+

Kapena kuchotsa moyo wanga limodzi ndi anthu achiwawa.*

10 Amene manja awo amachita khalidwe lochititsa manyazi,

Ndipo mʼdzanja lawo lamanja mwadzaza ziphuphu.

11 Koma ine, ndidzapitiriza kuchita zinthu mokhulupirika.

Ndipulumutseni* ndipo mundikomere mtima.

12 Phazi langa laima pamalo otetezeka.+

Ndidzatamanda Yehova mumpingo* waukulu.+

Salimo la Davide.

27 Yehova ndi kuwala kwanga+ komanso ndi amene amandipulumutsa.

Ndingaope ndani?+

Yehova ali ngati malo amene amateteza moyo wanga.+

Ndingachite mantha ndi ndani?

 2 Anthu oipa atandiukira kuti adye mnofu wanga,+

Adani angawo ndi amene anapunthwa nʼkugwa.

 3 Ngakhale gulu lankhondo litamanga msasa kuti lindiukire,

Mtima wanga sudzachita mantha.+

Ngakhale nkhondo yolimbana ndi ine itayambika,

Pameneponso ndidzadalira Mulungu.

 4 Ndapempha chinthu chimodzi kwa Yehova,

Chimenecho ndi chimene ndikuchilakalaka.

Chinthu chake nʼchakuti, ndikhale mʼnyumba ya Yehova masiku onse a moyo wanga,+

Kuti ndione ubwino wa Yehova,

Komanso kuti ndiyangʼane kachisi wake* moyamikira.*+

 5 Chifukwa pa tsiku la tsoka, adzandibisa mʼmalo ake otetezeka.+

Adzandibisa mʼmalo obisika a mutenti yake.+

Adzandiika pamwamba, pathanthwe.+

 6 Tsopano ndapambana pamaso pa adani anga onse amene andizungulira.

Ndidzapereka nsembe patenti yake ndikufuula mosangalala.

Ndidzaimba nyimbo zotamanda Yehova.

 7 Inu Yehova, ndimvetsereni pamene ndikuitana.+

Ndikomereni mtima ndipo mundiyankhe.+

 8 Mtima wanga wandikumbutsa za lamulo lanu lakuti:

“Funafunani nkhope yanga anthu inu.”

Ndidzafunafuna nkhope yanu, inu Yehova.+

 9 Musandibisire nkhope yanu.+

Musabweze mtumiki wanu mutakwiya.

Inu ndi amene mumandithandiza.+

Musanditaye kapena kundisiya, inu Mulungu amene mumandipulumutsa.

10 Ngakhale bambo anga ndi mayi anga atandisiya,+

Yehova adzanditenga.+

11 Ndilangizeni, inu Yehova, kuti ndiyende mʼnjira yanu.+

Nditsogolereni mʼnjira yoyenera kuti nditetezeke kwa adani anga.

12 Musandipereke kwa adani anga,+

Chifukwa mboni zabodza zikundinamizira mlandu,+

Ndipo akundiopseza kuti andichitira zachiwawa.

13 Kodi ndikanakhala ndili kuti ndikanapanda kukhala ndi chikhulupiriro

Choti ndidzaona ubwino wa Yehova mʼdziko la anthu amoyo?*+

14 Yembekezera Yehova.+

Limba mtima ndipo uchite zinthu mwamphamvu.+

Inde, yembekezera Yehova.

Salimo la Davide.

28 Ndikuitana inu Yehova, Thanthwe langa,+

Musatseke makutu anu pamene ine ndikuitana.

Mukakhala chete pamene ndikukuitanani,

Ndidzafanana ndi anthu amene akutsikira kudzenje la manda.+

 2 Imvani mawu anga ochonderera pamene ndikufuulira inu kuti mundithandize,

Pamene ndikukweza manja anga, nditayangʼana kumene kuli chipinda chamkati chamʼmalo anu opatulika.+

 3 Musandikokolole pamodzi ndi anthu oipa, amene amachita zopweteka anzawo,+

Anthu amene amalankhula mawu amtendere ndi anzawo, koma mʼmitima yawo muli zinthu zoipa.+

 4 Muwabwezere mogwirizana ndi zochita zawo,+

Mogwirizana ndi zochita zawo zoipa.

Abwezereni mogwirizana ndi ntchito za manja awo,

Mogwirizana ndi zimene achita.+

 5 Chifukwa iwo sachita chidwi ndi zochita za Yehova,+

Kapena ntchito za manja ake.+

Mulungu adzawagwetsa ndipo sadzawamanga.

 6 Atamandike Yehova,

Chifukwa iye wamva kuchonderera kwanga kopempha thandizo.

 7 Yehova ndi mphamvu yanga+ komanso chishango changa.+

Mtima wanga umamukhulupirira.+

Iye wandithandiza, moti mtima wanga ukusangalala.

Choncho ndidzamutamanda ndi nyimbo yanga.

 8 Yehova ndi mphamvu kwa anthu ake,

Iye ndi malo achitetezo, amapereka chipulumutso chachikulu kwa wodzozedwa wake.+

 9 Pulumutsani anthu anu, ndipo dalitsani cholowa chanu.+

Mukhale mʼbusa wawo ndipo muwanyamule mʼmanja mwanu mpaka kalekale.+

Nyimbo ya Davide.

29 Mʼpatseni Yehova zimene akuyenera kulandira, inu ana a amphamvu,

Mʼpatseni Yehova zimene akuyenera kulandira chifukwa cha ulemerero ndi mphamvu zake.+

 2 Mʼpatseni Yehova ulemerero woyenera dzina lake.

Weramirani* Yehova mutavala zovala zopatulika zokongola.*

 3 Mawu a Yehova akumveka pamwamba pa madzi,

Mawu a Mulungu waulemerero akugunda ngati bingu.+

Yehova ali pamwamba pa madzi ambiri.+

 4 Mawu a Yehova ndi amphamvu,+

Mawu a Yehova ndi aulemerero.

 5 Mawu a Yehova akuthyola mitengo ya mkungudza,

Inde, Yehova akuthyolathyola mitengo ya mkungudza ya ku Lebanoni.+

 6 Iye akuchititsa Lebanoni* kuti adumphedumphe ngati mwana wa ngʼombe,

Komanso Sirioni+ kuti adumphedumphe ngati mwana wa ngʼombe yakutchire.

 7 Yehova akamalankhula, mphenzi zimangʼanima.+

 8 Mawu a Yehova akuchititsa kuti chipululu chiphiriphithe,+

Yehova akuchititsa kuti chipululu cha Kadesi+ chiphiriphithe.

 9 Mawu a Yehova akuchititsa kuti mbawala zazikazi ziphiriphithe kenako nʼkubereka

Ndipo akuchititsa kuti munkhalango mukhale mopanda chilichonse.+

Ndipo onse mʼkachisi wake akunena kuti: “Ulemerero!”

10 Yehova wakhala pampando wake wachifumu pamwamba pa madzi osefukira,*+

Yehova ndi Mfumu ndipo adzalamulira mpaka kalekale.+

11 Yehova adzapatsa anthu ake mphamvu.+

Yehova adzadalitsa anthu ake powapatsa mtendere.+

Nyimbo yotsegulira nyumba. Salimo la Davide.

30 Ndidzakutamandani inu Yehova, chifukwa mwandipulumutsa.*

Simunalole kuti adani anga asangalale chifukwa cha mavuto anga.+

 2 Inu Yehova Mulungu wanga, ndinafuulira kwa inu kuti mundithandize ndipo munandichiritsa.+

 3 Inu Yehova, mwanditulutsa mʼManda,*+

Mwandisunga ndi moyo, mwanditeteza kuti ndisatsikire mʼdzenje.*+

 4 Imbani nyimbo zotamanda Yehova, inu okhulupirika ake,+

Yamikani dzina* lake loyera.+

 5 Chifukwa mkwiyo wa Mulungu sukhalitsa pa munthu,+

Koma munthu amene wasangalala naye* amamukomera mtima kwa moyo wake wonse.+

Munthu akhoza kulira usiku, koma mʼmawa amafuula mosangalala.+

 6 Pa nthawi imene ndinalibe mavuto ndinanena kuti:

“Sindidzagwedezeka.”*

 7 Inu Yehova, pa nthawi imene munkasangalala nane,* munachititsa kuti ndikhale wamphamvu ngati phiri.+

Koma mutabisa nkhope yanu, ndinachita mantha.+

 8 Ndinapitiriza kuitana inu Yehova,+

Ndipo ndinapitiriza kuchonderera Yehova kuti andikomere mtima.

 9 Kodi imfa yanga ili* ndi phindu lanji? Kodi pali phindu lanji ngati nditatsikira kudzenje la manda?+

Kodi fumbi lingakutamandeni?+ Kodi lingalengeze kuti inu ndinu wokhulupirika?+

10 Imvani inu Yehova, ndipo mundikomere mtima.+

Inu Yehova, ndithandizeni.+

11 Mwasintha kulira kwanga kuti kukhale kuvina.

Mwandivula chiguduli changa ndipo mwandiveka chisangalalo,

12 Kuti ndiimbe nyimbo zokutamandani ndipo ndisakhale chete.

Inu Yehova Mulungu wanga, ndidzakutamandani mpaka kalekale.

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ya Davide.

31 Ndathawira kwa inu Yehova.+

Musalole kuti ndichite manyazi.+

Ndipulumutseni chifukwa cha chilungamo chanu.+

 2 Tcherani khutu lanu* kwa ine.

Ndilanditseni mofulumira.+

Mukhale malo anga otetezeka apaphiri,

Mukhale malo a mpanda wolimba kuti mundipulumutse.+

 3 Chifukwa inu ndinu thanthwe langa ndi malo anga achitetezo.+

Chifukwa cha dzina lanu,+ mudzanditsogolera ndi kundilozera njira.+

 4 Mudzandipulumutsa mu ukonde umene anditchera mwachinsinsi,+

Chifukwa inu ndinu malo anga achitetezo.+

 5 Ndikupereka mzimu wanga mʼmanja mwanu.+

Mwandiwombola, inu Yehova Mulungu wa choonadi.*+

 6 Ndimadana ndi anthu amene amadzipereka kwa mafano achabechabe komanso opanda pake.

Koma ine ndimadalira Yehova.

 7 Ndidzasangalala kwambiri chifukwa cha chikondi chanu chokhulupirika,

Chifukwa mwaona kusautsika kwanga.+

Mukudziwa mavuto aakulu amene ndili nawo.*

 8 Simunandipereke mʼmanja mwa adani,

Koma mwachititsa kuti ndiime pamalo otetezeka.*

 9 Ndikomereni mtima inu Yehova, chifukwa ndavutika kwambiri.

Maso anga afooka chifukwa cha chisoni,+ chimodzimodzinso thupi langa lonse.*+

10 Moyo wanga ndi wodzaza ndi chisoni+

Ndipo zaka za moyo wanga nʼzodzaza ndi kubuula.+

Mphamvu zanga zikuchepa chifukwa cha zolakwa zanga,

Mafupa anga afooka.+

11 Adani anga onse amandinyoza,+

Makamaka anthu oyandikana nawo.

Ndipo anthu ondidziwa amachita nane mantha.

Akandiona ndili panja amandithawa.+

12 Iwo anandiiwala* ngati kuti ndinafa.

Ndili ngati chiwiya chosweka.

13 Ndamva mphekesera zambiri zoipa.

Ndikuchita mantha chifukwa ndikuopsezedwa kuchokera kumbali zonse.+

Akasonkhana pamodzi kuti alimbane nane,

Amakonza chiwembu kuti achotse moyo wanga.+

14 Koma ine ndimakhulupirira inu Yehova.+

Ndipo ndikunena kuti: “Inu ndinu Mulungu wanga.”+

15 Moyo wanga uli* mʼmanja mwanu.

Ndilanditseni mʼmanja mwa adani anga komanso kwa anthu amene akundizunza.+

16 Ndikomereni mtima, ine mtumiki wanu.+

Ndipulumutseni ndi chikondi chanu chokhulupirika.

17 Inu Yehova, musalole kuti ndichite manyazi pamene ndikukuitanani.+

Anthu oipa achite manyazi.+

Apite ku Manda* ndipo akhale chete.+

18 Milomo yonena mabodza isowe chonena,+

Milomo imene imalankhula modzikweza komanso monyoza wolungama.

19 Ubwino wanu ndi wochuluka kwambiri!+

Ubwino umenewu mwasungira anthu amene amakuopani,+

Ndipo mwausonyeza kwa anthu amene amathawira kwa inu, pamaso pa anthu onse.+

20 Mudzawabisa mʼmalo otetezeka pafupi ndi inu,+

Kuwachotsa kwa anthu amene awakonzera chiwembu.

Mudzawabisa mʼmalo anu otetezeka

Kuti anthu amene akuwanyoza asawapeze.*+

21 Yehova atamandike,

Chifukwa mʼnjira yodabwitsa, wandisonyeza chikondi chokhulupirika+ mumzinda umene wazunguliridwa ndi adani.+

22 Koma ine ndinapanikizika nʼkunena kuti:

“Ndifa ndipo simudzandionanso.”+

Koma inu munamva kuchonderera kwanga kopempha thandizo pamene ndinafuulira kwa inu.+

23 Kondani Yehova, inu nonse amene muli okhulupirika kwa iye!+

Yehova amateteza okhulupirika,+

Koma aliyense wodzikuza amamulanga kwambiri.+

24 Limbani mtima ndipo muchite zinthu mwamphamvu,+

Inu nonse amene mukuyembekezera Yehova.+

Salimo la Davide. Masikili.*

32 Wosangalala ndi munthu amene zolakwa zake zakhululukidwa, amene machimo ake akhululukidwa.+

 2 Wosangalala ndi munthu amene Yehova sakumuona kuti ndi wolakwa,+

Amene alibe mtima wachinyengo.

 3 Pamene ndinakhala chete osaulula machimo anga, mafupa anga anafooka, chifukwa ndinkavutika mumtima mwanga tsiku lonse.+

 4 Dzanja lanu linkandilemera* masana ndi usiku.+

Mphamvu zanga zinauma* ngati madzi mʼnyengo yotentha yachilimwe. (Selah)

 5 Pamapeto pake ndinaulula tchimo langa kwa inu,

Sindinabise cholakwa changa.+

Ndinati: “Ndidzaulula machimo anga kwa Yehova.”+

Ndipo inu munandikhululukira zolakwa zanga ndi machimo anga.+ (Selah)

 6 Nʼchifukwa chake aliyense wokhulupirika adzapemphera kwa inu+

Mwayi wokuyandikirani udakalipo.+

Akatero ngakhale madzi osefukira sadzamupeza.

 7 Ndinu malo anga obisalamo,

Mudzanditeteza ku mavuto.+

Mwachititsa kuti ndizunguliridwe ndi anthu amene akufuula mosangalala chifukwa chakuti mwandipulumutsa.+ (Selah)

 8 Inu munati: “Ndidzakupatsa nzeru komanso kukulangiza njira yoti uyendemo.+

Ndidzakupatsa malangizo ndi kukuyangʼanira.+

 9 Anthu inu, musakhale ngati hatchi kapena nyulu* yosazindikira,+

Imene munthu amachita kuimanga chingwe pakamwa pake kuti athetse kupulupudza kwake,

Akatero mʼpamene imatha kumuyandikira.”

10 Zopweteka za woipa ndi zambiri.

Koma wokhulupirira Yehova amatetezedwa ndi chikondi Chake chokhulupirika.+

11 Inu olungama, kondwerani chifukwa cha zimene Yehova wachita ndipo sangalalani.

Fuulani mosangalala inu nonse owongoka mtima.

33 Fuulani mosangalala chifukwa cha Yehova,+ olungama inu.

Mʼpoyenera kuti olungama atamande Mulungu.

 2 Yamikani Yehova poimba zeze.

Muimbireni nyimbo zomutamanda ndi choimbira cha zingwe 10.

 3 Muimbireni nyimbo yatsopano.+

Imbani mwaluso choimbira cha zingwe ndipo muzifuula mosangalala.

 4 Chifukwa mawu a Yehova ndi oona,+

Ndipo chilichonse chimene amachita ndi chodalirika.

 5 Iye amakonda chilungamo ndipo amaweruza mosakondera.+

Dziko lapansi ladzaza ndi chikondi chokhulupirika cha Yehova.+

 6 Kumwamba kunalengedwa ndi mawu a Yehova,+

Ndipo analenga zinthu zonse zakumwamba* ndi mpweya wamʼkamwa mwake.

 7 Amasonkhanitsa madzi amʼnyanja ngati damu,+

Amaika madzi amphamvu mʼnyumba zosungiramo zinthu.

 8 Dziko lonse lapansi liope Yehova.+

Anthu onse okhala panthaka ya dziko lapansi achite naye mantha.

 9 Chifukwa iye analankhula ndipo zinachitika.+

Iye analamula ndipo zinakhalapo.+

10 Yehova wasokoneza zolinga za mitundu ya anthu.+

Walepheretsa mapulani* a mitundu ya anthu.+

11 Koma zolinga za Yehova zidzakhalapo mpaka kalekale.+

Maganizo amumtima mwake adzakhalapo ku mibadwomibadwo.

12 Wosangalala ndi mtundu umene Mulungu wawo ndi Yehova,+

Anthu amene iye wawasankha kuti akhale cholowa chake.+

13 Yehova amayangʼana padziko lapansi, kuchokera kumwamba.

Iye amaona ana onse a anthu.+

14 Kuchokera kumalo amene amakhala,

Amayangʼanitsitsa anthu amene akukhala padziko lapansi.

15 Iye ndi amene amaumba mitima ya anthu onse,

Ndipo amafufuza ntchito zawo zonse.+

16 Palibe mfumu imene inapulumuka chifukwa cha kukula kwa gulu lake lankhondo.+

Munthu wamphamvu sapulumuka chifukwa cha kuchuluka kwa mphamvu zake.+

17 Si nzeru kudalira hatchi chifukwa singapulumutse munthu,+

Mphamvu zake zochuluka sizingapulumutse munthu

18 Taonani! Diso la Yehova limayangʼana anthu amene amamuopa,+

Amene amayembekezera chikondi chake chokhulupirika,

19 Kuti awapulumutse ku imfa,

Komanso kuwathandiza kuti akhale ndi moyo pa nthawi ya njala.+

20 Tikuyembekezera Yehova.

Iye ndi amene amatithandiza komanso ndi chishango chathu.+

21 Mulungu amachititsa kuti mitima yathu isangalale,

Chifukwa timadalira dzina lake loyera.+

22 Inu Yehova, chikondi chanu chokhulupirika chikhale pa ife,+

Pamene tikupitiriza kuyembekezera inu.+

Salimo la Davide, pa nthawi imene anachita zinthu ngati wamisala+ pamaso pa Abimeleki, moti anamuthamangitsa ndipo Davideyo anathawa.

א [Aleph]

34 Ndidzatamanda Yehova nthawi zonse.

Sindidzasiya kumutamanda ndi pakamwa panga.

ב [Beth]

 2 Monyadira, ndidzapereka ulemu kwa Yehova.*+

Ofatsa adzamva ndipo adzasangalala.

ג [Gimel]

 3 Lemekezani Yehova pamodzi ndi ine,+

Tiyeni tonse tikweze dzina lake.

ד [Daleth]

 4 Ndinapemphera kwa Yehova ndipo iye anandiyankha.+

Anandipulumutsa ku zinthu zonse zimene zimandichititsa mantha.+

ה [He]

 5 Amene anamukhulupirira anasangalala,

Ndipo nkhope zawo sizinachite manyazi.

ז [Zayin]

 6 Munthu wonyozekayu anaitana ndipo Yehova anamva.

Anamupulumutsa ku mavuto ake onse.+

ח [Heth]

 7 Mngelo wa Yehova amamanga msasa kuzungulira anthu onse amene amaopa Mulungu,+

Ndipo amawapulumutsa.+

ט [Teth]

 8 Talawani ndipo muona kuti Yehova ndi wabwino.+

Wosangalala ndi munthu amene amathawira kwa iye.

י [Yod]

 9 Opani Yehova, inu oyera ake onse,

Chifukwa onse amene amamuopa sasowa kanthu.+

כ [Kaph]

10 Ngakhale mikango yamphamvu* ingakhale ndi njala chifukwa chosowa chakudya.

Koma anthu amene akufunafuna Yehova sadzasowa chilichonse chabwino.+

ל [Lamed]

11 Bwerani kuno ana anga, ndimvetsereni.

Ndikuphunzitsani kuopa Yehova.+

מ [Mem]

12 Kodi ndi ndani pakati panu amene amakonda moyo,

Ndipo angakonde atakhala ndi moyo wabwino kwa masiku ambiri?+

נ [Nun]

13 Ndiyetu muteteze lilime lanu ku zinthu zoipa,+

Komanso milomo yanu kuti isalankhule chinyengo.+

ס [Samekh]

14 Siyani kuchita zinthu zoipa ndipo muzichita zabwino.+

Yesetsani kukhala mwamtendere ndi ena komanso kuulimbikitsa.+

ע [Ayin]

15 Maso a Yehova ali pa olungama,+

Ndipo makutu ake amamva kufuula kwawo kopempha thandizo.+

פ [Pe]

16 Koma Yehova amakwiyira anthu ochita zoipa,

Iye adzawawononga ndipo sadzakumbukiridwanso padziko lapansi.+

צ [Tsade]

17 Olungama anafuula ndipo Yehova anamva,+

Iye anawapulumutsa mʼmavuto awo onse.+

ק [Qoph]

18 Yehova ali pafupi ndi anthu a mtima wosweka.+

Iye amapulumutsa anthu amene akudzimvera chisoni mumtima mwawo.*+

ר [Resh]

19 Mavuto* a munthu wolungama ndi ambiri,+

Koma Yehova amamupulumutsa ku mavuto onsewo.+

ש [Shin]

20 Amateteza mafupa onse a munthu wolungamayo.

Ndipo palibe fupa ngakhale limodzi limene lathyoledwa.+

ת [Taw]

21 Munthu woipa adzakumana ndi tsoka ndipo adzafa.

Anthu odana ndi munthu wolungama adzapezeka olakwa.

22 Yehova amawombola moyo wa atumiki ake.

Palibe aliyense wothawira kwa iye amene adzapezeke wolakwa.+

Salimo la Davide.

35 Inu Yehova, nditetezeni kwa anthu amene akundiimba mlandu.+

Menyanani ndi anthu amene akumenyana ndi ine.+

 2 Tengani chishango chanu chachingʼono ndi chachikulu,+

Ndipo nyamukani ndi kunditeteza.+

 3 Tengani mkondo ndi nkhwangwa yapankhondo kuti mulimbane ndi adani anga amene akundithamangitsa.+

Ndiuzeni kuti:* “Ine ndine chipulumutso chako.”+

 4 Amene akufunafuna moyo wanga achite manyazi komanso anyozeke.+

Amene akukonza chiwembu choti andiphe abwerere mwamanyazi.

 5 Akhale ngati mankhusu* ouluzika ndi mphepo,

Mngelo wa Yehova awathamangitse.+

 6 Njira yawo ikhale yamdima ndi yoterera

Pamene mngelo wa Yehova akuwathamangitsa.

 7 Popanda chifukwa, iwo atchera ukonde kuti andikole.

Akumba dzenje kuti ndigweremo ngakhale kuti sindinalakwe.

 8 Tsoka liwagwere modzidzimutsa,

Akodwe mu ukonde umene atchera okha.

Agweremo nʼkufa.+

 9 Koma ine ndidzakondwera chifukwa cha zimene Yehova wachita.

Ndidzasangalala chifukwa wandipulumutsa.

10 Ndinena ndi mtima wanga wonse kuti:

“Inu Yehova, ndi ndani angafanane ndi inu?

Mumapulumutsa anthu ovutika mʼmanja mwa anthu amphamvu kuposa iwowo.+

Mumapulumutsa anthu ovutika komanso anthu osauka kwa anthu amene akuwalanda zinthu zawo.”+

11 Mboni zoipa mtima zabwera,+

Ndipo zikundifunsa zinthu zimene sindikuzidziwa.

12 Iwo amandibwezera zoipa mʼmalo mwa zabwino,+

Ndipo ndimakhala wachisoni ngati namfedwa.

13 Koma akadwala ndinkavala chiguduli,

Ndinkasala kudya posonyeza kudzichepetsa.

Ndipo pemphero langa likapanda kuyankhidwa,

14 Ndinkayendayenda ndikulira ngati kuti ndikulira maliro a mnzanga kapena mchimwene wanga,

Ndinkawerama chifukwa cha chisoni ngati munthu amene akulira maliro a mayi ake.

15 Koma nditapunthwa anasangalala ndipo anasonkhana pamodzi.

Anasonkhana pamodzi kuti andibisalire nʼkundiukira.

Anandikhadzulakhadzula ndipo sanakhale chete.

16 Anthu osaopa Mulungu akundinyoza mwachipongwe,

Iwo akundikukutira mano.+

17 Inu Yehova, kodi mudzayangʼanira zimenezi mpaka liti?+

Ndipulumutseni kuti asandiphe,+

Pulumutsani moyo wanga,* womwe ndi wamtengo wapatali, kwa mikango yamphamvu.*+

18 Mukatero, ndidzakuyamikirani mumpingo waukulu.+

Ndidzakutamandani pakati pa anthu ambiri.

19 Musalole kuti anthu amene amadana nane popanda chifukwa+ asangalale chifukwa cha mavuto anga.

Musalole kuti anthu amene amadana nane popanda chifukwa andipsinyire diso mondinyoza.+

20 Chifukwa iwo salankhula mwamtendere,

Koma mwachinyengo, amakonzera chiwembu anthu okonda mtendere amʼdzikoli.+

21 Iwo amatsegula kwambiri pakamwa pawo kuti atsutsane nane,

Iwo amati: “Eya! Eya! Taona tokha ndi maso athuwa.”

22 Inu Yehova, mwaona zimenezi. Choncho musakhale chete.+

Inu Yehova, musakhale kutali ndi ine.+

23 Khalani tcheru ndipo nyamukani ndi kunditeteza,

Inu Mulungu wanga Yehova, nditetezeni pa mlandu wanga.

24 Inu Yehova Mulungu wanga, mundiweruze mogwirizana ndi mfundo zanu zolungama,+

Musalole kuti adani anga asangalale chifukwa cha mavuto anga.

25 Musalole kuti mumtima mwawo anene kuti: “Eya! Tapeza zimene timafuna.”

Ndipo asanene kuti: “Tamumeza.”+

26 Onsewo achite manyazi nʼkuthedwa nzeru,

Onse amene amasangalala tsoka likandigwera.

Onse amene amadzikweza pamaso panga atsitsidwe ndipo achite manyazi.

27 Koma amene amakonda chilungamo changa afuule mosangalala.

Nthawi zonse azinena kuti:

“Alemekezeke Yehova, amene amasangalala mtumiki wake akakhala pamtendere.”+

28 Ndipo lilime langa lidzafotokoza* za chilungamo chanu,+

Komanso kukutamandani tsiku lonse.+

Kwa wotsogolera nyimbo. Salimo la Davide, mtumiki wa Yehova.

36 Uchimo umalankhula mumtima mwa munthu woipa, nʼkumuuza zochita.

Maso ake saona chifukwa choopera Mulungu.+

 2 Iye amadziona kuti ndi wofunika kwambiri,

Moti sazindikira zolakwa zake nʼkudana nazo.+

 3 Mawu apakamwa pake ndi opweteka komanso achinyengo.

Iye amasonyeza kuti alibe nzeru zomuthandiza kuchita zinthu zabwino.

 4 Ngakhale ali pabedi lake, amakonza chiwembu kuti apweteke anzake.

Amayenda panjira yoipa,

Ndipo sapewa kuchita zinthu zoipa.

 5 Inu Yehova, chikondi chanu chokhulupirika chafika kumwamba.+

Kukhulupirika kwanu kwafika mpaka mʼmitambo.

 6 Chilungamo chanu chili ngati mapiri akuluakulu.*+

Ziweruzo zanu zili ngati madzi ambiri ozama.+

Inu Yehova, mumapulumutsa munthu ndiponso nyama.+

 7 Inu Mulungu, chikondi chanu chokhulupirika ndi chamtengo wapatali!+

Ana a anthu amabisala mumthunzi wa mapiko anu.+

 8 Amamwa zakumwa zabwino* zamʼnyumba yanu nʼkukhuta.+

Ndipo mumawachititsa kuti amwe zinthu zanu zosangalatsa zimene zimayenda ngati mtsinje.+

 9 Inu ndinu kasupe wa moyo.+

Chifukwa cha kuwala kochokera kwa inu, timaona kuwala.+

10 Pitirizani kusonyeza chikondi chanu chokhulupirika kwa anthu amene amakudziwani,+

Ndiponso chilungamo chanu kwa anthu owongoka mtima.+

11 Musalole kuti phazi la anthu odzikweza lindipondereze

Kapena kuti dzanja la anthu oipa lindithamangitse.

12 Onani, anthu ochita zoipa agwa.

Awagwetsera pansi ndipo sangathenso kudzuka.+

Salimo la Davide.

א [Aleph]

37 Usakhumudwe* chifukwa cha anthu oipa

Kapena kuchitira nsanje anthu ochita zoipa.+

 2 Iwo adzafota mwamsanga ngati udzu+

Ndipo adzanyala ngati msipu wobiriwira.

ב [Beth]

 3 Uzikhulupirira Yehova ndipo uzichita zabwino.+

Ukhale padziko lapansi* ndipo uzichita zinthu mokhulupirika.+

 4 Uzisangalala* chifukwa cha Yehova,

Ndipo adzakupatsa zimene mtima wako umalakalaka.

ג [Gimel]

 5 Lola kuti Yehova akutsogolere panjira yako,*+

Uzimudalira ndipo iye adzakuthandiza.+

 6 Iye adzachititsa kuti kulungama kwako kuwale ngati mʼmawa,

Ndipo chilungamo chako adzachichititsa kuti chiwale ngati dzuwa masana.

ד [Daleth]

 7 Khala chete pamaso pa Yehova+

Ndipo umuyembekezere moleza mtima.

Usakhumudwe ndi munthu

Amene amakonza ziwembu nʼkuzikwaniritsa popanda vuto lililonse.+

ה [He]

 8 Usapse mtima ndipo uzipewa kukwiya.+

Usapse mtima nʼkuchita zoipa.*

 9 Chifukwa anthu oipa adzaphedwa,+

Koma amene akuyembekezera Yehova adzalandira dziko lapansi.+

ו [Waw]

10 Kwatsala kanthawi kochepa, ndipo oipa sadzakhalaponso.+

Udzayangʼana pamene ankakhala,

Ndipo sadzapezekapo.+

11 Koma anthu ofatsa adzalandira dziko lapansi,+

Ndipo adzasangalala ndi mtendere wochuluka.+

ז [Zayin]

12 Munthu woipa amakonzera chiwembu munthu wolungama,+

Ndipo amamukukutira mano.

13 Koma Yehova adzamuseka,

Chifukwa akudziwa kuti mapeto ake adzafika.+

ח [Heth]

14 Oipa asolola malupanga awo ndipo akunga mauta* awo,

Kuti agwetse oponderezedwa ndi osauka,

Kuti aphe anthu amene njira zawo ndi zolungama.

15 Koma lupanga lawo lidzalasa mtima wawo womwe,+

Mauta awo adzathyoledwa.

ט [Teth]

16 Zinthu zochepa zimene munthu wolungama ali nazo ndi zabwino

Kusiyana ndi zinthu zochuluka za anthu ambiri oipa.+

17 Chifukwa manja a anthu oipa adzathyoledwa,

Koma Yehova adzathandiza anthu olungama.

י [Yod]

18 Yehova amadziwa mavuto amene anthu osalakwa akukumana nawo,*

Ndipo cholowa chawo chidzakhalapo mpaka kalekale.+

19 Pa nthawi ya tsoka sadzachita manyazi,

Ndipo pa nthawi ya njala adzakhala ndi chakudya chochuluka.

כ [Kaph]

20 Koma oipa onse adzatheratu,+

Adani a Yehova adzasowa mofulumira ngati malo okongola odyetsera ziweto amene msipu wake wobiriwira suchedwa kufota.

Iwo adzatha mofulumira ngati utsi.

ל [Lamed]

21 Munthu woipa amabwereka zinthu za ena koma osabweza,

Koma wolungama amakhala wowolowa manja* ndipo amagawira ena zinthu zake.+

22 Anthu amene Mulungu wawadalitsa adzalandira dziko lapansi,

Koma amene wawatemberera adzaphedwa.+

מ [Mem]

23 Yehova akasangalala ndi njira za munthu+

Amamusonyeza zoyenera kuchita pa moyo wake.+

24 Ngakhale atapunthwa, sadzagweratu,+

Chifukwa Yehova wamugwira dzanja kuti amuthandize.*+

נ [Nun]

25 Ndinali mwana ndipo tsopano ndakula,

Koma sindinaonepo munthu aliyense wolungama atasiyidwa,+

Kapena ana ake akupemphapempha chakudya.+

26 Nthawi zonse amakongoza ena zinthu zake mokoma mtima,+

Ndipo ana ake adzalandira madalitso.

ס [Samekh]

27 Pewani kuchita zoipa ndipo muzichita zabwino,+

Mukatero mudzakhala padziko lapansi mpaka kalekale.

28 Chifukwa Yehova amakonda chilungamo,

Ndipo sadzasiya anthu ake okhulupirika.+

ע [Ayin]

Adzawateteza nthawi zonse.+

Koma mbadwa za anthu oipa zidzaphedwa.+

29 Olungama adzalandira dziko lapansi,+

Ndipo adzakhala mmenemo mpaka kalekale.+

פ [Pe]

30 Pakamwa pa munthu wolungama pamalankhula zinthu zanzeru,*

Ndipo lilime lake limalankhula zinthu zachilungamo.+

31 Chilamulo cha Mulungu wake chili mumtima mwake.+

Iye adzachitsatira nthawi zonse.+

צ [Tsade]

32 Woipa amayangʼanitsitsa munthu wolungama,

Ndipo amafuna kuti amuphe.

33 Koma Yehova sadzasiya wolungama mʼmanja mwa woipayo+

Kapena kumupeza wolakwa akamaweruzidwa.+

ק [Qoph]

34 Yembekezera Yehova ndi kutsatira njira zake,

Ndipo adzakukweza kuti ulandire dziko lapansi.

Oipa akamadzaphedwa,+ iwe udzaona.+

ר [Resh]

35 Ine ndaona munthu wankhanza komanso woipa

Zinthu zikumuyendera bwino ngati mtengo wa masamba obiriwira bwino panthaka yake.+

36 Koma anafa mwadzidzidzi ndipo sanapezekenso.+

Ndinamufunafuna ndipo sindinamupeze.+

ש [Sin]

37 Onani munthu wosalakwa,*

Ndipo yangʼanitsitsani munthu wolungama,+

Chifukwa tsogolo la munthu ameneyo lidzakhala lamtendere.+

38 Koma anthu onse ochimwa adzawonongedwa.

Mʼtsogolo, anthu oipa adzaphedwa.+

ת [Taw]

39 Chipulumutso cha anthu olungama chimachokera kwa Yehova.+

Iye ndi malo awo achitetezo champhamvu pa nthawi ya mavuto.+

40 Yehova adzawathandiza nʼkuwapulumutsa.+

Adzawalanditsa kwa oipa nʼkuwapulumutsa,

Chifukwa athawira kwa iye.+

Nyimbo ya Davide ya chikumbutso.

38 Inu Yehova, musandidzudzule mutakwiya,

Kapena kundilangiza mutapsa mtima.+

 2 Chifukwa mivi yanu yandilasa kwambiri mpaka mkati,

Ndipo dzanja lanu likundilemera.+

 3 Thupi langa lonse likudwala* chifukwa cha mkwiyo wanu.

Mʼmafupa anga mulibe mtendere chifukwa cha tchimo langa.+

 4 Chifukwa zolakwa zanga zakwera kupitirira mutu wanga.+

Sindingathe kuzisenza chifukwa zikulemera kwambiri ngati katundu wolemera.

 5 Zilonda zanga zanyeka komanso zikununkha

Chifukwa cha kupusa kwanga.

 6 Ndili ndi nkhawa komanso chisoni chachikulu.

Ndikuyendayenda ndili wachisoni tsiku lonse.

 7 Ndikumva kuwotcha mʼthupi mwanga,*

Thupi langa lonse likudwala.+

 8 Thupi langa lonse lachita dzanzi ndipo ndilibiretu mphamvu.

Ndikubuula mokweza* chifukwa cha kuvutika kwa mtima wanga.

 9 Inu Yehova, mukudziwa zinthu zonse zimene ndikulakalaka,

Nthawi zonse mumamva ndikamadandaula.

10 Mtima wanga ukugunda kwambiri komanso mphamvu zanga zatha,

Ndipo maso anga achita mdima.+

11 Anzanga komanso anthu amene ndimawakonda akundisala chifukwa cha mliri wanga,

Ndipo anthu oyandikana nawo sakufuna kukhala nane pafupi.

12 Anthu amene akufunafuna moyo wanga anditchera misampha,

Amene akufuna kundivulaza akukambirana zoti andiwononge,+

Tsiku lonse iwo amapanga pulani yoti andinamize.

13 Koma ine ndakhala ngati munthu wogontha ndipo sindikumvetsera,+

Ndakhala ngati munthu wosalankhula ndipo sindikutsegula pakamwa.+

14 Ndakhala ngati munthu wosamva,

Amene sangalankhule chilichonse podziteteza.

15 Chifukwa ine ndinayembekezera inu Yehova.+

Ndipo inu Yehova Mulungu wanga, munandiyankha.+

16 Ine ndinati: “Musalole kuti adani anga asangalale chifukwa cha mavuto anga

Kapena kuti adzikweze ngati phazi langa litaterereka.”

17 Chifukwa ndinali nditatsala pangʼono kugwa,

Ndipo ndinkamva ululu nthawi zonse.+

18 Ndinaulula cholakwa changa.+

Tchimo langa linkandisowetsa mtendere.+

19 Koma adani anga ndi amphamvu kwambiri,

Ndipo odana nane popanda chifukwa anachuluka.

20 Iwo anandibwezera choipa mʼmalo mwa chabwino,

Ndikafuna kuchita zabwino iwo ankandiletsa.

21 Inu Yehova, musandisiye.

Inu Mulungu, musakhale kutali ndi ine.+

22 Bwerani mwamsanga mudzandithandize,

Inu Yehova, amene mumandipulumutsa.+

Kwa wotsogolera nyimbo. Aimbe nyimboyi pa Yedutuni.*+ Nyimbo ya Davide.

39 Ine ndinanena kuti: “Ndidzakhala wosamala ndi zochita zanga

Kuti ndisachimwe ndi lilime langa.+

Ndidzaphimba pakamwa panga kuti ndisalankhule+

Nthawi zonse pamene woipa ali pamaso panga.”

 2 Ndinakhala chete osalankhula kanthu.+

Sindinalankhule kanthu ngakhale kokhudza zinthu zabwino,

Koma ululu wanga unali waukulu.

 3 Mumtima mwanga munayaka moto.*

Ndili mkati moganizira,* moto unapitiriza kuyaka.

Kenako ndinanena kuti:

 4 “Inu Yehova, ndithandizeni kuzindikira kuti moyo wanga ndi waufupi,

Komanso kudziwa chiwerengero cha masiku anga,+

Kuti ndidziwe kuti moyo wanga ndi waufupi bwanji.*

 5 Ndithudi, mwachepetsa masiku a moyo wanga,+

Ndipo masiku a moyo wanga si kanthu pamaso panu.+

Ndithudi, munthu aliyense ngakhale ataoneka kuti ndi wotetezeka, amangokhala ngati mpweya.+ (Selah)

 6 Zoonadi, moyo wa munthu aliyense umangodutsa ngati chithunzithunzi.

Iye amangovutika* popanda phindu.

Amaunjika chuma, osadziwa kuti amene adzasangalale nacho ndi ndani.+

 7 Ndiyeno inu Yehova, kodi ine ndikuyembekezera chiyani?

Chiyembekezo changa ndi inu nokha.

 8 Ndipulumutseni ku zolakwa zanga zonse.+

Musalole kuti munthu wopusa azindinyoza.

 9 Ndinakhala chete.

Sindinatsegule pakamwa panga,+

Chifukwa inu ndi amene munachita zimenezi.+

10 Ndichotsereni mliri umene mwandigwetsera.

Mphamvu zanga zatha chifukwa inu mwandipatsa chilango.

11 Mumathandiza munthu kuti asinthe pomupatsa chilango chifukwa cha zolakwa zake.+

Mumawononga zinthu zake zamtengo wapatali ngati mmene njenjete* imachitira.

Ndithudi, munthu aliyense ali ngati mpweya.+ (Selah)

12 Imvani pemphero langa, inu Yehova,

Mvetserani pamene ndikulira kupempha thandizo.+

Musanyalanyaze misozi yanga.

Chifukwa ndine mlendo kwa inu,+

Mlendo wongodutsa mofanana ndi makolo anga onse.+

13 Musandiyangʼane mutakwiya, kuti ndikhalenso wosangalala

Ndisanamwalire nʼkuiwalika.”

Kwa wotsogolera nyimbo. Salimo la Davide.

40 Ndinayembekezera Yehova ndi mtima wonse,*

Ndipo iye anatchera khutu* kwa ine nʼkumva kulira kwanga kopempha thandizo.+

 2 Iye ananditulutsa mʼdzenje la madzi a mkokomo,

Ananditulutsa mʼchithaphwi cha matope.

Ndipo anapondetsa phazi langa pathanthwe,

Anachititsa kuti ndiyende panthaka yolimba.

 3 Kenako anaika nyimbo yatsopano mʼkamwa mwanga,+

Nyimbo yotamanda Mulungu wathu.

Ambiri adzaona zimenezi ndipo adzachita mantha,

Nʼkuyamba kukhulupirira Yehova.

 4 Wosangalala ndi munthu amene amakhulupirira Yehova

Komanso amene sadalira anthu otsutsa kapena anthu amene amakhulupirira mabodza.*

 5 Inu Yehova Mulungu wanga,

Mwatichitira zinthu zambiri zodabwitsa+

Ndipo mumatiganizira.+

Palibe angafanane ndi inu.

Nditati ndilankhule kapena kunena za zodabwitsazo,

Zingakhale zochuluka kwambiri moti sindingathe kuzifotokoza.+

 6 Nsembe zanyama komanso nsembe zina, simunazifune.*+

Koma munatsegula makutu anga kuti ndimve.+

Simunapemphe nsembe zopsereza ndi nsembe zamachimo.+

 7 Ndiyeno ine ndinati: “Taonani, ine ndabwera.

Mumpukutu* munalembedwa za ine.+

 8 Ndimasangalala* kuchita zimene mumafuna, inu Mulungu wanga,+

Ndipo chilamulo chanu chili mumtima mwanga.+

 9 Ndimalengeza uthenga wabwino wa chilungamo mumpingo waukulu.+

Onani! Sinditseka pakamwa panga,+

Monga mmene mukudziwira, Inu Yehova.

10 Sindibisa chilungamo chanu mumtima mwanga.

Ndimalengeza kuti ndinu wokhulupirika komanso kuti mumapulumutsa atumiki anu.

Sindibisa chikondi chanu chokhulupirika komanso choonadi chanu mumpingo waukulu.”+

11 Inu Yehova, musasiye kundisonyeza chifundo.

Chikondi chanu chokhulupirika komanso choonadi chanu zizinditeteza nthawi zonse.+

12 Masoka amene andizungulira ndi ambiri moti sindingathe kuwawerenga.+

Zolakwa zanga ndi zochuluka moti sindikutha kuona kumene ndikulowera.+

Zachuluka kwambiri kuposa tsitsi lakumutu kwanga,

Ndipo ndataya mtima.

13 Mukhale wofunitsitsa kundipulumutsa, inu Yehova.+

Ndithandizeni mofulumira, inu Yehova.+

14 Onse amene akufuna kuchotsa moyo wanga

Achititsidwe manyazi komanso anyozeke.

Amene akusangalala ndi tsoka langa

Abwerere mwamanyazi.

15 Onse amene akunena kuti: “Eyaa! Eyaa!”

Achite mantha kwambiri chifukwa cha zinthu zochititsa manyazi zimene ziwachitikire.

16 Koma amene akufunafuna inu,+

Akondwere ndi kusangalala chifukwa choti akudziwani.+

Amene amasangalala ndi njira imene mumapulumutsira anthu, nthawi zonse azinena kuti:

“Yehova alemekezeke.”+

17 Koma ine ndine munthu wovutika komanso wosauka.

Yehova aone zimene zikundichitikira.

Inu ndi amene mumandithandiza komanso kundipulumutsa.+

Inu Mulungu wanga, musachedwe.+

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ya Davide.

41 Wosangalala ndi munthu amene amachita zinthu moganizira munthu wonyozeka.+

Pa tsiku la tsoka, Yehova adzamupulumutsa.

 2 Yehova adzamuteteza nʼkusunga moyo wake.

Anthu ena adzaona kuti akusangalala,+

Ndipo Mulungu sadzamupereka kwa adani ake.*+

 3 Yehova adzathandiza munthu woganizira wonyozekayo pamene akudwala pabedi lake.+

Mudzamusamalira bwino kwambiri pa nthawi imene akudwala.

 4 Ine ndinati: “Inu Yehova, ndikomereni mtima.+

Ndichiritseni,+ chifukwa ndakuchimwirani.”+

 5 Koma adani anga amanena zoipa zokhudza ine kuti:

“Kodi ameneyu afa liti kuti dzina lake liiwalike?”

 6 Mmodzi wa iwo akabwera kudzandiona, sanena zinthu moona mtima.

Amasonkhanitsa nkhani zoipa.

Akatero amachoka nʼkukafalitsa nkhani zoipazo.

 7 Onse amene amadana nane akunongʼonezana zokhudza ine.

Akupangana zoti andichitire chiwembu. Iwo akuti:

 8 “Chinthu chochititsa mantha chamuchitikira.

Tsopano popeza iye ali chigonere, sadzadzukanso.”+

 9 Ngakhale munthu amene ndinkakhala naye mwamtendere, amene ndinkamukhulupirira,+

Munthu amene ankadya chakudya changa, watukula chidendene chake nʼkundiukira.+

10 Koma inu Yehova, ndikomereni mtima nʼkundidzutsa,

Kuti ndiwapatse chilango chifukwa cha zimene anachita.

11 Mdani wanga akapanda kundigonjetsa nʼkufuula mosangalala,

Ndidzadziwa kuti mukusangalala nane.+

12 Koma ine mumandithandiza chifukwa choti ndine wokhulupirika,+

Ndipo mudzasangalala nane mpaka kalekale.*+

13 Atamandike Yehova Mulungu wa Isiraeli,

Kuyambira panopo mpaka kalekale.*+

Ame! Ame!

BUKU LACHIWIRI

(Masalimo 42-72)

Kwa wotsogolera nyimbo. Masikili* ya ana a Kora.+

42 Mofanana ndi mbawala imene imalakalaka mitsinje ya madzi,

Inenso* ndikulakalaka inu Mulungu.

 2 Mofanana ndi munthu amene akulakalaka madzi, ndikulakalaka* Mulungu, Mulungu wamoyo.+

Ndidzapita liti kukaonekera pamaso pa Mulungu?*+

 3 Misozi yanga ili ngati chakudya changa masana ndi usiku.

Anthu amandinyoza tsiku lonse kuti: “Mulungu wako ali kuti?”+

 4 Ndikukumbukira zinthu zimenezi ndipo mtima wanga ukupweteka kwambiri.

Chifukwa poyamba ndinkayenda ndi gulu lalikulu la anthu,

Ndinkayenda pangʼonopangʼono patsogolo pawo kupita kunyumba ya Mulungu,

Gulu la anthu likuimba mosangalala nyimbo zoyamika Mulungu,

Pa nthawi ya chikondwerero.+

 5 Nʼchifukwa chiyani ndataya mtima?+

Nʼchifukwa chiyani ndikuvutika mumtima mwanga?

Ndidzayembekezera Mulungu,+

Ndidzamutamanda chifukwa iye ndi Mpulumutsi wanga Wamkulu.+

 6 Inu Mulungu wanga, ine ndataya mtima.+

Nʼchifukwa chake ndakukumbukirani,+

Pamene ndili mʼdziko la Yorodano ndi mʼmapiri a Herimoni,

Pamene ndili mʼPhiri la Mizara.*

 7 Madzi akuya akufuulira madzi akuya

Kudzera mumkokomo wa mathithi anu.

Mafunde anu onse amphamvu andimiza.+

 8 Masana Yehova adzandisonyeza chikondi chake chokhulupirika,

Ndipo usiku ndidzamuimbira nyimbo, ndidzapemphera kwa Mulungu amene amandipatsa moyo.+

 9 Ndidzauza Mulungu, thanthwe langa kuti:

“Nʼchifukwa chiyani mwandiiwala?+

Kodi ndiziyenda wachisoni chifukwa chiyani? Nʼchifukwa chiyani adani anga akundipondereza?”+

10 Anthu amene amadana nane kwambiri akundinyoza,*

Amandinyoza tsiku lonse kuti: “Mulungu wako ali kuti?”+

11 Nʼchifukwa chiyani ndataya mtima?

Nʼchifukwa chiyani ndikuvutika mumtima mwanga?

Ndidzayembekezera Mulungu,+

Ndidzamutamanda chifukwa iye ndi Mpulumutsi wanga Wamkulu komanso Mulungu wanga.+

43 Ndiweruzeni inu Mulungu,+

Nditetezeni pa mlandu wanga+ wotsutsana ndi mtundu wosakhulupirika.

Ndipulumutseni kwa munthu wachinyengo komanso wochita zinthu zopanda chilungamo.

 2 Inu ndinu Mulungu wanga, ndinu malo anga achitetezo.+

Nʼchifukwa chiyani mwanditaya?

Kodi ndiziyenda wachisoni chifukwa chiyani? Nʼchifukwa chiyani adani anga akundipondereza?+

 3 Tumizani kuwala kwanu ndi choonadi chanu.+

Zimenezi zinditsogolere.+

Zinditsogolere kuphiri lanu lopatulika ndi kuchihema chanu chachikulu.+

 4 Kenako ndidzapita paguwa lansembe la Mulungu,+

Kwa Mulungu amene amandisangalatsa kwambiri.

Ndipo ndidzakutamandani ndi zeze+ inu Mulungu, Mulungu wanga.

 5 Nʼchifukwa chiyani ndataya mtima?

Nʼchifukwa chiyani ndikuvutika mumtima mwanga?

Ndidzayembekezera Mulungu,+

Ndidzamutamanda chifukwa iye ndi Mpulumutsi wanga Wamkulu komanso Mulungu wanga.+

Kwa wotsogolera nyimbo. Salimo la ana a Kora.+ Masikili.*

44 Inu Mulungu, ife tamva ndi makutu athu,

Makolo athu anatifotokozera+

Ntchito zimene inu munachita mu nthawi yawo,

Mʼmasiku akale.

 2 Munathamangitsa anthu a mitundu ina ndi dzanja lanu,+

Ndipo dziko lawo munalipereka kwa makolo athu.+

Munagonjetsa mitundu ya anthu nʼkuithamangitsa.+

 3 Iwo sanatenge dzikolo pogwiritsa ntchito lupanga lawo.+

Ndipo si mkono wawo umene unachititsa kuti apambane.+

Koma zimenezi zinatheka chifukwa cha dzanja lanu lamanja,+ mkono wanu ndi kuwala kwa nkhope yanu,

Chifukwa munkasangalala nawo.+

 4 Inu Mulungu, ndinu Mfumu yanga.+

Lamulani kuti Yakobo apambane.*

 5 Ndi mphamvu zanu tidzathamangitsa adani athu.+

Mʼdzina lanu tidzagonjetsa anthu amene akutiukira.+

 6 Chifukwa sindidalira uta wanga,

Ndipo lupanga langa silingandipulumutse.+

 7 Ndi inu amene munatipulumutsa kwa adani athu,+

Ndi inu amene munachititsa manyazi anthu amene amadana nafe.

 8 Tidzatamanda Mulungu tsiku lonse,

Ndipo tidzatamanda dzina lanu mpaka kalekale. (Selah)

 9 Koma tsopano mwatitaya ndipo mwatichititsa manyazi,

Simukutsogoleranso magulu athu ankhondo.

10 Mukuchititsa kuti tizithawa pamaso pa adani athu.+

Anthu amene amadana nafe amatenga chilichonse chimene akufuna.

11 Mwatipereka kwa adani athu kuti atidye ngati nkhosa,

Ndipo mwatimwaza pakati pa anthu a mitundu ina.+

12 Mwagulitsa anthu anu pamtengo wotsika kwambiri,+

Ndipo simunapeze phindu pamalonda amenewo.*

13 Mwachititsa kuti anthu oyandikana nafe azititonza,

Komanso kuti anthu onse amene atizungulira azitinyoza ndi kutiseka.

14 Mwachititsa kuti anthu amitundu ina azitinyoza,*+

Komanso kuti anthu azitipukusira mitu.

15 Ndimachita manyazi tsiku lonse,

Ndipo nkhope yanga yagwa chifukwa cha manyazi,

16 Chifukwa cha mawu a anthu amene akunditonza ndi kulankhula zachipongwe,

Ndiponso chifukwa cha mdani wathu amene akufuna kutibwezera zoipa.

17 Zonsezi zatigwera, koma sitinakuiwaleni,

Ndipo sitinaphwanye pangano lanu.+

18 Mitima yathu sinakhale yosakhulupirika,

Ndipo mapazi athu sanapatuke panjira yanu.

19 Koma inu mwatiphwanya kumalo amene mimbulu imakhala,

Mwatiphimba ndi mdima wandiweyani.

20 Ngati tinaiwala dzina la Mulungu wathu,

Kapena ngati tinapemphera kwa mulungu wachilendo titakweza manja athu,

21 Kodi Mulungu sakanadziwa zimenezi?

Iye amadziwa zinsinsi zamumtima.+

22 Chifukwa cha inu, tikuphedwa nthawi zonse.

Takhala ngati nkhosa zokaphedwa.+

23 Dzukani. Nʼchifukwa chiyani mukugonabe, inu Yehova?+

Dzukani. Musatitaye kwamuyaya.+

24 Nʼchifukwa chiyani mukubisa nkhope yanu?

Nʼchifukwa chiyani mukuiwala mavuto athu ndi kuponderezedwa kwathu?

25 Atigwetsera pafumbi.

Matupi athu ali thasa! padothi.+

26 Nyamukani kuti mutithandize+

Tipulumutseni* chifukwa cha chikondi chanu chokhulupirika.+

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimboyi iimbidwe motsatira kaimbidwe ka “Nyimbo ya Maluwa.” Salimo la ana a Kora. Masikili.*+ Nyimbo yachikondi.

45 Mtima wanga wasangalala kwambiri chifukwa cha nkhani yosangalatsa.

Ine ndikuti: “Nyimbo yangayi ikunena za* mfumu.”+

Lilime langa likhale ngati cholembera+ cha wokopera Malemba* waluso.+

 2 Ndiwe wokongola kwambiri pakati pa ana a anthu.

Mʼkamwa mwako mumatuluka mawu osangalatsa.+

Nʼchifukwa chake Mulungu wakudalitsa mpaka kalekale.+

 3 Mangirira lupanga lako+ mʼchiuno mwako wamphamvu iwe,+

Utavala ulemu ndiponso ulemerero.+

 4 Upite mu ulemerero wako ndipo upambane.*+

Kwera pahatchi yako chifukwa cha choonadi, kudzichepetsa ndi chilungamo,+

Ndipo dzanja lako lamanja lidzachita* zinthu zochititsa mantha.

 5 Mivi yako ndi yakuthwa ndipo ikuchititsa kuti anthu agwe pamaso pako.+

Imalasa mitima ya adani a mfumu.+

 6 Mulungu ndi mpando wako wachifumu mpaka kalekale.+

Ndodo ya ufumu wako ndi ndodo yachilungamo.+

 7 Unkakonda chilungamo+ ndipo unkadana ndi zoipa.+

Nʼchifukwa chake Mulungu, Mulungu wako, wakudzoza+ ndi mafuta achisangalalo+ chachikulu kuposa mafumu anzako.

 8 Zovala zako zonse ndi zothiridwa mafuta onunkhira a mule, aloye ndi kasiya.*

Umasangalala ndi nyimbo zoimbidwa ndi zipangizo za zingwe, kuchokera mʼchinyumba chachikulu cha mfumu, chokongoletsedwa ndi minyanga ya njovu.

 9 Ana aakazi a mafumu ali mʼgulu la akazi amene umawalemekeza.

Mkazi wamkulu wa mfumu waima* kudzanja lako lamanja atavala zovala zagolide wa ku Ofiri.+

10 Mvetsera, iwe mwana wanga wamkazi. Mvetsera mwatcheru ndipo utchere khutu.

Uiwale anthu ako ndi nyumba ya bambo ako.

11 Mfumu idzalakalaka kukongola kwako,

Chifukwa ndi mbuye wako,

Choncho iweramire.

12 Mwana wamkazi wa ku Turo adzabwera ndi mphatso.

Amuna olemera kwambiri adzafuna kuti uwakomere mtima.

13 Mwana wamkazi wa mfumu ali pa ulemerero waukulu mʼnyumba ya mfumu.

Zovala zake ndi zokongoletsedwa* ndi golide.

14 Adzamubweretsa kwa mfumu atavala zovala zokongola.*

Anamwali anzake omuperekeza akuwabweretsa kwa iwe.

15 Adzawabweretsa akusangalala ndi kukondwera.

Ndipo adzalowa mʼnyumba ya mfumu.

16 Ana anu adzatenga malo a makolo anu,

Ndipo mudzawaika kuti akhale akalonga padziko lonse lapansi.+

17 Ndidzachititsa kuti anthu adziwe dzina lanu mʼmibadwo yonse yamʼtsogolo.+

Nʼchifukwa chake mitundu ya anthu idzakutamandani mpaka kalekale.

Kwa wotsogolera nyimbo. Salimo la ana a Kora.+ Mogwirizana ndi kaimbidwe ka Alamoti.* Nyimbo.

46 Mulungu ndi pothawira pathu komanso mphamvu yathu,+

Thandizo lopezeka mosavuta pa nthawi ya mavuto.+

 2 Nʼchifukwa chake sitidzaopa, ngakhale dziko lapansi litasintha,

Ndiponso ngakhale mapiri atagwera mʼnyanja yakuya nʼkumira,+

 3 Ngakhale madzi amʼnyanjayo atawinduka nʼkuchita thovu,+

Ndiponso ngakhale mapiri atagwedezeka chifukwa cha kuwinduka kwa nyanjayo. (Selah)

 4 Pali mtsinje umene nthambi zake zimachititsa kuti anthu amumzinda wa Mulungu asangalale,+

Chihema chachikulu chopatulika cha Wamʼmwambamwamba.

 5 Mulungu ali mumzindawo+ ndipo sungagonjetsedwe.

Mulungu adzauthandiza mʼbandakucha.+

 6 Mitundu ya anthu inachita phokoso, maufumu anagonjetsedwa.

Iye analankhula mokweza mawu ndipo dziko lapansi linasungunuka.+

 7 Yehova wa magulu ankhondo akumwamba ali ndi ife.+

Mulungu wa Yakobo ndi malo athu othawirako otetezeka.* (Selah)

 8 Bwerani mudzaone ntchito za Yehova,

Mmene wachitira zinthu zodabwitsa padziko lapansi.

 9 Akuthetsa nkhondo padziko lonse lapansi.+

Wathyola uta ndi kupindapinda mkondo.

Ndipo wawotcha pamoto magaleta ankhondo.*

10 “Gonjerani ndipo mudziwe kuti ine ndine Mulungu.

Ndidzakwezedwa pakati pa mitundu ya anthu,+

Ndidzakwezedwa padziko lapansi.”+

11 Yehova wa magulu ankhondo akumwamba ali ndi ife.+

Mulungu wa Yakobo ndi malo athu othawirako otetezeka.+ (Selah)

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ndi Salimo la ana a Kora.+

47 Inu anthu nonse, ombani mʼmanja.

Fuulani mosangalala chifukwa Mulungu wapambana.

 2 Chifukwa Yehova, Wamʼmwambamwamba ndi wochititsa mantha,+

Iye ndi Mfumu yaikulu padziko lonse lapansi.+

 3 Iye amagonjetsa mitundu ya anthu kuti tiziilamulira.

Amaika mitundu ya anthu pansi pa mapazi athu.+

 4 Amatisankhira cholowa,+

Chimene Yakobo, amene amamukonda, amasangalala nacho.+ (Selah)

 5 Mulungu wakwera kumalo ake, anthu akufuula mosangalala,

Yehova wakwera kumalo ake, anthu akuliza lipenga la nyanga ya nkhosa.

 6 Imbani nyimbo zotamanda Mulungu, imbani nyimbo zotamanda.

Imbani nyimbo zotamanda Mfumu yathu, imbani nyimbo zotamanda.

 7 Chifukwa Mulungu ndi Mfumu ya dziko lonse lapansi.+

Imbani nyimbo zotamanda ndiponso sonyezani kuti ndinu ozindikira.

 8 Mulungu wakhala Mfumu ya mitundu ya anthu.+

Mulungu wakhala pampando wake wachifumu wopatulika.

 9 Atsogoleri a mitundu ya anthu asonkhana pamodzi

Ndi anthu a Mulungu wa Abulahamu.

Chifukwa Mulungu ali ndi mphamvu pa olamulira a* dziko lapansi.

Iye ndi wokwezeka kwambiri.+

Nyimbo ndi Salimo la ana a Kora.+

48 Yehova ndi wamkulu komanso woyenera kutamandidwa kwambiri,

Mumzinda wa Mulungu wathu, mʼphiri lake loyera.

 2 Phiri la Ziyoni limene lili mʼdera lakutali lakumpoto,

Ndi lokongola chifukwa lili pamalo okwezeka komanso anthu padziko lonse lapansi akusangalala nalo,+

Ndipo ndi mzinda wa Mfumu Yaikulu.+

 3 Munsanja zake zokhala ndi mpanda wolimba,

Mulungu wasonyeza kuti iye ndi malo othawirako otetezeka.*+

 4 Taonani! Mafumu asonkhana,*

Onse pamodzi abwera.

 5 Iwo ataona mzindawo, anadabwa.

Anapanikizika nʼkuthawa mwamantha.

 6 Kumeneko iwo anayamba kunjenjemera,

Anavutika ngati mkazi amene akubereka.

 7 Pogwiritsa ntchito mphepo yamphamvu yakumʼmawa, munaswa sitima za ku Tarisi.

 8 Zimene tinangomva, tsopano taziona tokha,

Mumzinda wa Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, mumzinda wa Mulungu wathu.

Mulungu adzakhazikitsa mzindawo mpaka kalekale.+ (Selah)

 9 Inu Mulungu, ife timaganizira mozama za chikondi chanu chokhulupirika,+

Tili mʼkachisi wanu.

10 Inu Mulungu, mofanana ndi dzina lanu, mawu okutamandani

Afika kumalire a dziko lapansi.+

Dzanja lanu lamanja ladzaza ndi chilungamo.+

11 Phiri la Ziyoni likondwere,+

Matauni* a ku Yuda asangalale chifukwa cha zigamulo zanu.+

12 Gubani mozungulira Ziyoni. Zungulirani mzinda wonsewo,

Werengani nsanja zake.+

13 Ganizirani mofatsa za mpanda wake wolimba.+

Yenderani nsanja zake zokhala ndi mpanda wolimba,

Kuti mudzafotokozere mibadwo yamʼtsogolo.

14 Chifukwa Mulungu uyu ndi Mulungu wathu+ mpaka muyaya.

Iye adzatitsogolera mpaka kalekale.*+

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ndi Salimo la ana a Kora.+

49 Mvetserani izi, anthu nonsenu.

Tcherani khutu anthu nonse okhala mʼdzikoli,*

 2 Onyozeka ndi olemekezeka omwe,

Olemera komanso osauka.

 3 Pakamwa panga padzalankhula zinthu zanzeru,

Ndipo zimene ndikuganizira mozama mumtima mwanga+ zidzasonyeza kuti ndine wozindikira.

 4 Ndidzatchera khutu kuti ndimvetsere mwambi.

Ndidzamasulira mawu anga ophiphiritsa poimba zeze.

 5 Sindidzachita mantha pa nthawi yamavuto,+

Pamene anthu oipa andizungulira kuti andivulaze.

 6 Anthu amene akukhulupirira chuma chawo,+

Amene amadzitamandira chifukwa cha kuchuluka kwa chuma chawo,+

 7 Palibe ngakhale mmodzi wa iwo amene angathe kuwombola mʼbale wake,

Kapena kumuperekera dipo kwa Mulungu,+

 8 (Ndipo malipiro owombolera moyo* wawo ndi amtengo wapatali,

Moti sangakwanitse kuwapereka),

 9 Kuti akhale ndi moyo mpaka kalekale osaona dzenje la manda.+

10 Aliyense amaona kuti ngakhale anthu anzeru amafa,

Munthu wopusa komanso munthu wopanda nzeru, onse amawonongeka,+

Ndipo chuma chawo amasiyira anthu ena.+

11 Zimene mtima wawo umalakalaka nʼzakuti nyumba zawo zikhale mpaka kalekale,

Matenti awo akhale ku mibadwomibadwo.

Ndipo malo awo amawapatsa mayina awo.

12 Koma munthu, ngakhale kuti ndi wolemekezeka, sadzapitiriza kukhala ndi moyo mpaka kalekale.+

Iye amangofanana ndi nyama zimene zimafa.+

13 Izi ndi zimene zimachitikira anthu opusa,+

Komanso anthu amene amawatsatira, amene amasangalala ndi mawu awo opanda pake. (Selah)

14 Iwo adzafa ngati nkhosa zimene zikupita kokaphedwa.

Imfa idzakhala mʼbusa wawo.

Mʼmawa anthu owongoka mtima adzawalamulira.+

Matupi awo adzawonongeka.+

Kwawo kudzakhala ku Manda*+ osati mʼnyumba yachifumu.+

15 Koma Mulungu adzandiwombola ku mphamvu ya* Manda,*+

Chifukwa adzandigwira dzanja. (Selah)

16 Musachite mantha chifukwa chakuti munthu wina walemera,

Kapena chifukwa chakuti katundu wamʼnyumba mwake wawonjezeka,

17 Chifukwa akadzamwalira sadzatenga china chilichonse.+

Ulemerero wake sadzapita nawo limodzi.+

18 Chifukwa pamene anali moyo ankatamanda moyo wake.+

(Anthu amakutamanda ukalemera.)+

19 Koma pamapeto pake amafa ngati mmene makolo ake anachitira.

Iwo sadzaonanso kuwala.

20 Munthu amene sazindikira zimenezi, ngakhale atakhala wolemekezeka,+

Amangofanana ndi nyama zimene zimafa.

Nyimbo ya Asafu.+

50 Yehova, Mulungu wa milungu+ walankhula.

Iye akuitana anthu onse okhala padziko lapansi,

Kuchokera kotulukira dzuwa mpaka kumene limalowera.*

 2 Mulungu wawala ali ku Ziyoni, mzinda wokongola kwambiri.+

 3 Mulungu wathu adzabwera ndipo sangakhale chete.+

Pamaso pake pali moto wowononga,+

Ndipo pamalo onse omuzungulira pali chimphepo chamkuntho.+

 4 Akuitana kumwamba ndi dziko lapansi+

Kuti aweruze anthu ake. Iye akuti:+

 5 “Sonkhanitsani okhulupirika anga kwa ine,

Amene akuchita pangano ndi ine pogwiritsa ntchito nsembe.”+

 6 Kumwamba kukulengeza kuti iye ndi wachilungamo,

Chifukwa Mulungu ndi Woweruza.+ (Selah)

 7 “Ndimvereni anthu anga, ndipo ine ndilankhula,

Inu Aisiraeli, ine ndipereka umboni wotsutsana nanu.+

Ine ndine Mulungu, Mulungu wanu.+

 8 Sindikukudzudzulani chifukwa cha nsembe zanu,

Kapena chifukwa cha nsembe zanu zopsereza zathunthu zimene mumapereka kwa ine nthawi zonse.+

 9 Sindikuyenera kutenga ngʼombe yamphongo mʼnyumba yanu,

Kapena mbuzi* mʼmakola anu.+

10 Chifukwa nyama iliyonse yakutchire ndi yanga,+

Ngakhale nyama zopezeka mʼmapiri 1,000.

11 Ndikudziwa mbalame iliyonse ya mʼmapiri,+

Nyama zosawerengeka zakutchire ndi zanga.

12 Ngakhale nditakhala ndi njala, sindingakuuzeni,

Chifukwa dziko lonse ndiponso zonse zimene zili mmenemo ndi zanga.+

13 Kodi ndiyenera kudya nyama ya ngʼombe zamphongo

Kapena kumwa magazi a mbuzi?+

14 Yamikani Mulungu kuti ikhale ngati nsembe imene mukupereka kwa iye,+

Ndipo perekani kwa Wamʼmwambamwamba zimene mwalonjeza.+

15 Pa nthawi yamavuto mundiitane.+

Ine ndidzakupulumutsani, ndipo inu mudzandilemekeza.”+

16 Koma Mulungu adzauza woipa kuti:

“Ndi ndani wakupatsa udindo wofotokoza malangizo anga,+

Kapena wolankhula za pangano langa?+

17 Iwe umadana ndi chilango,*

Ndipo sumamvera mawu anga.*+

18 Ukaona wakuba umasangalala ndi zochita zake.*+

Ndipo umagwirizana ndi anthu achigololo.

19 Umagwiritsa ntchito pakamwa pako kufalitsa zinthu zoipa,

Ndipo lilime lako limalankhula zachinyengo.+

20 Umakhala pansi nʼkumanenera mʼbale wako zinthu zoipa,+

Umaulula zolakwa za* mwana wamwamuna wa mayi ako.

21 Utachita zinthu zimenezi, ine sindinalankhule kanthu,

Choncho unkaganiza kuti ndikuona zinthu ngati mmene iweyo ukuzionera.

Koma tsopano ndikudzudzula

Ndipo ndikuuza mlandu umene ndakupeza nawo.+

22 Ganizirani zinthu zimenezi, anthu oiwala Mulungu inu,+

Kuti ndisakukhadzulekhadzuleni popanda aliyense wokupulumutsani.

23 Amene akundiyamikira kuti ikhale nsembe imene akupereka kwa ine akundilemekeza.+

Ndipo munthu amene akupitiriza kuchita zabwino,

Ndidzamuonetsa chipulumutso changa.”+

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ya Davide, pa nthawi imene mneneri Natani anapita kwa iye, Davideyo atagona ndi Bati-seba.+

51 Ndikomereni mtima inu Mulungu, mogwirizana ndi chikondi chanu chokhulupirika.+

Fufutani zolakwa zanga mogwirizana ndi chifundo chanu chachikulu.+

 2 Mundisambitse bwinobwino nʼkuchotsa cholakwa changa,+

Ndiyeretseni ku tchimo langa.+

 3 Chifukwa zolakwa zanga ndikuzidziwa bwino,

Ndipo tchimo langa lili pamaso panga* nthawi zonse.+

 4 Inuyo ndi amene ndakuchimwirani kwambiri kuposa aliyense.*+

Ndachita chinthu chimene mumachiona kuti ndi choipa.+

Choncho mukamalankhula, mumalankhula zachilungamo,

Ndipo mukamaweruza, mumaweruza mwachilungamo.+

 5 Taonani! Ndinabadwa ndili wochimwa,

Ndipo ndine wochimwa kuchokera pamene mayi anga anatenga pakati panga.+

 6 Taonani! Mumasangalala ndi choonadi chochokera pansi pa mtima.+

Ndiphunzitseni* kuti ndikhale ndi mtima wanzeru.

 7 Ndiyeretseni ndi hisope* ku machimo anga kuti ndikhale woyera.+

Ndisambitseni kuti ndiyere kwambiri kuposa matalala.+

 8 Ndichititseni kumva kufuula kokondwera ndi kosangalala,

Kuti ndisangalale ngakhale kuti mwathyola mafupa anga.+

 9 Ndikhululukireni* machimo anga,+

Ndipo fufutani* zolakwa zanga zonse.+

10 Inu Mulungu, lengani mtima wolungama mkati mwanga,+

Ndipo sinthani mmene ndimaganizira+ kuti ndikhale wokhulupirika.

11 Musandichotse pamaso panu nʼkunditaya.

Ndipo musandichotsere mzimu wanu woyera.

12 Bwezeretsani mwa ine chisangalalo chimene chimabwera chifukwa cha chipulumutso chanu.+

Ndipatseni mtima wofunitsitsa kukumverani.*

13 Anthu olakwa ndidzawaphunzitsa njira zanu,+

Kuti ochimwawo abwerere kwa inu.

14 Inu Mulungu, ndipulumutseni ku mlandu wa magazi,+ inu Mulungu wa chipulumutso changa,+

Kuti lilime langa lilengeze mosangalala kuti ndinu wolungama.+

15 Inu Yehova, tsegulani milomo yangayi,

Kuti pakamwa panga patamande inu.+

16 Chifukwa nsembe simukuifuna, mukanakhala kuti mukuifuna ndikanaipereka kwa inu.+

Inu simusangalala ndi nsembe yopsereza yathunthu.+

17 Nsembe zimene Mulungu amasangalala nazo ndi kudzimvera chisoni mumtima.

Inu Mulungu, simudzakana* mtima wosweka ndi wophwanyika.+

18 Chitirani Ziyoni zabwino mwa kukoma mtima kwanu.

Ndipo mangani mpanda wa Yerusalemu.

19 Mukatero mudzasangalala ndi nsembe zachilungamo,

Mudzakondwera ndi nsembe zopsereza komanso nsembe zathunthu.

Pamenepo ngʼombe zamphongo zidzaperekedwa paguwa lanu la nsembe.+

Kwa wotsogolera nyimbo. Masikili.* Salimo la Davide, pa nthawi imene Doegi wa ku Edomu, anapita kwa Sauli nʼkukamuuza kuti Davide wapita kunyumba ya Ahimeleki.+

52 Nʼchifukwa chiyani ukudzitukumula chifukwa cha zinthu zoipa zimene ukuchita, wamphamvu iwe?+

Chikondi chokhulupirika cha Mulungu nʼchokhalitsa.+

 2 Lilime lako limene ndi lakuthwa ngati lezala,+

Limakonza chiwembu komanso kuchita zachinyengo.+

 3 Umakonda kwambiri zinthu zoipa kuposa zabwino,

Umakonda kwambiri kunama kuposa kulankhula zoona. (Selah)

 4 Umakonda mawu onse opweteka ena,

Iwe amene lilime lako limalankhula zachinyengo.

 5 Nʼchifukwa chake Mulungu adzakugwetsa ndipo sudzakhalakonso.+

Adzakugwira nʼkukukokera kutali ndi tenti yako,+

Ndipo adzakuzula nʼkukuchotsa mʼdziko la anthu amoyo.+ (Selah)

 6 Olungama adzaona zimenezi nʼkuchita mantha,+

Ndipo adzamuseka+ kuti:

 7 “Taonani, munthu uyu sanadalire Mulungu monga malo ake othawirako,*+

Koma ankadalira chuma chake chochuluka,+

Komanso ziwembu zimene ankapanga.”*

 8 Koma ine ndidzakhala ngati mtengo waukulu wa maolivi wa masamba obiriwira mʼnyumba ya Mulungu.

Ndidzadalira chikondi chokhulupirika cha Mulungu+ mpaka kalekale.

 9 Ndidzakutamandani mpaka kalekale, chifukwa cha zimene mwachita.+

Pamaso pa okhulupirika anu,

Ndidzayembekezera dzina lanu,+ chifukwa ndi labwino.

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimboyi iimbidwe potsatira kaimbidwe ka Mahalati.* Masikili.* Salimo la Davide.

53 Munthu wopusa* amanena mumtima mwake kuti:

“Kulibe Yehova.”+

Zochita zopanda chilungamo za anthu amenewa ndi zoipa komanso zonyansa,

Ndipo palibe amene akuchita zabwino.+

 2 Koma kuchokera kumwamba, Mulungu amayangʼana ana a anthu,+

Kuti aone ngati pali aliyense wozindikira, ngati pali aliyense amene akufunafuna Yehova.+

 3 Onse apatuka,

Ndipo onsewo ndi achinyengo.

Palibe aliyense amene akuchita zabwino,

Palibiretu ndi mmodzi yemwe.+

 4 Kodi palibe aliyense womvetsa zinthu pakati pa anthu ochita zoipawa?

Iwo amadya anthu anga ngati kuti akudya chakudya.

Ndipo sapemphera kwa Yehova.+

 5 Koma adzagwidwa ndi mantha aakulu,

Mantha amene sanayambe agwidwapo chiyambire,*

Chifukwa Mulungu adzamwaza mafupa a anthu amene akukuukirani.*

Mudzawachititsa manyazi chifukwa Yehova wawakana.

 6 Zikanakhala bwino chipulumutso cha Isiraeli chikanachokera ku Ziyoni.+

Yehova akadzabwezeretsa anthu ake amene anagwidwa nʼkutengedwa kupita kudziko lina,

Yakobo adzasangalale, Isiraeli adzakondwere.

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimboyi iimbidwe ndi zipangizo za zingwe. Masikili.* Salimo la Davide. Pa nthawi imene amuna a ku Zifi anabwera kudzauza Sauli kuti: “Davide akubisala kwathu.”+

54 Inu Mulungu, ndipulumutseni mʼdzina lanu,+

Ndipo nditetezeni*+ ndi mphamvu zanu.

 2 Inu Mulungu, imvani pemphero langa.+

Tcherani khutu ku mawu ochokera mʼkamwa mwanga.

 3 Chifukwa anthu achilendo andiukira,

Ndipo anthu ankhanza akufunafuna moyo wanga.+

Iwo salemekeza Mulungu.*+ (Selah)

 4 Taonani! Mulungu ndi amene amandithandiza.+

Yehova amadalitsa anthu amene akundithandiza.

 5 Iye adzabwezera adani anga+ zoipa zimene akuchitira anthu ena.

Inu Mulungu wanga, awonongeni* chifukwa ndinu wokhulupirika.+

 6 Ndidzapereka nsembe kwa inu+ mofunitsitsa.

Inu Yehova, ndidzatamanda dzina lanu chifukwa ndi labwino.+

 7 Inu mumandipulumutsa pa mavuto anga onse,+

Ndipo ndidzayangʼana adani anga atagonja.+

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimboyi iimbidwe ndi zipangizo za zingwe. Masikili.* Salimo la Davide.

55 Inu Mulungu, mvetserani pemphero langa,+

Ndipo musanyalanyaze pempho langa lakuti mundichitire chifundo.*+

 2 Ndimvetsereni ndipo mundiyankhe.+

Mtima wanga suli mʼmalo chifukwa cha nkhawa zanga,+

Ndipo ndikuvutika mumtima mwanga

 3 Chifukwa cha zimene mdani wanga akunena

Komanso chifukwa chakuti woipa akundipanikiza.

Iwo andiunjikira mavuto,

Ndipo mwaukali akundisungira chidani.+

 4 Mtima wanga ukundipweteka kwambiri,+

Ndipo ndikuopa imfa.+

 5 Ndagwidwa ndi mantha ndipo ndikunjenjemera,

Komanso ndikunthunthumira.

 6 Nthawi zonse ndimanena kuti: “Ndikanakhala ndi mapiko ngati njiwa!

Ndikanaulukira kutali nʼkukakhala malo otetezeka.

 7 Ndikanathawira kutali.+

Ndikanapita kukakhala mʼchipululu.+ (Selah)

 8 Ndikanathawira kumalo otetezeka,

Kutali ndi mphepo yamphamvu, kutali ndi mphepo yamkuntho.”

 9 Inu Yehova, sokonezani anthu oipa, ndipo sokonezani mapulani awo,*+

Chifukwa ndaona zachiwawa ndi mikangano mumzinda.

10 Masana ndi usiku amayenda pamwamba pa mpanda kuzungulira mzindawo.

Ndipo mumzindawo muli chidani ndi mavuto.+

11 Mmenemo muli mavuto okhaokha.

Ndipo kuponderezana ndi chinyengo sizimachoka kubwalo la mzindawo.+

12 Chifukwa amene akundinyoza si mdani.+

Akanakhala mdani ndikanapirira.

Amene wandiukira si munthu wodana nane kwambiri.

Akanakhala munthu wodana nane kwambiri ndikanabisala.

13 Koma ndi iwe, munthu ngati ine ndemwe,*+

Mnzanga weniweni amene ndikumudziwa bwino.+

14 Tinali mabwenzi apamtima.

Tinkayenda limodzi ndi gulu la anthu kupita kunyumba ya Mulungu.

15 Iwo awonongedwe!+

Atsikire ku Manda* ali amoyo.

Chifukwa mʼmalo amene amakhala komanso mʼmitima yawo muli zoipa.

16 Koma ine ndidzafuulira Mulungu,

Ndipo Yehova adzandipulumutsa.+

17 Usiku, mʼmawa ndi masana ndimavutika ndipo ndimabuula,*+

Koma Mulungu amamva mawu anga.+

18 Iye adzandipulumutsa* kwa anthu amene akundiukira nʼkundipatsa mtendere,

Chifukwa gulu la anthu landiukira.+

19 Mulungu adzamva ndipo adzawapatsa chilango,+

Amene wakhala pampando wachifumu kuyambira kalekale.+ (Selah)

Iwo adzakana kusintha,

Anthu amene sanaope Mulungu.+

20 Iye* anaukira anthu amene anali naye pamtendere.+

Iye anaphwanya pangano lake.+

21 Mawu ake ndi osalala kuposa mafuta amumkaka,+

Koma mumtima mwake amakonda nkhondo.

Mawu ake ndi osalala kuposa mafuta,

Koma ali ngati malupanga akuthwa.+

22 Umutulire Yehova nkhawa zako,+

Ndipo iye adzakuthandiza.+

Iye sadzalola kuti munthu wolungama agwe.*+

23 Koma inu Mulungu, mudzatsitsira oipawo mʼdzenje lakuya.+

Anthu amene ali ndi mlandu wa magazi komanso achinyengowo, sadzakwanitsa kukhala ngakhale hafu ya moyo wawo.+

Koma ine ndidzakhulupirira inu.

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimboyi iimbidwe motsatira nyimbo ya “Nkhunda Imene Sinena Kanthu Ndipo Imakhala Kutali.” Salimo la Davide. Mikitamu.* Pa nthawi imene Afilisiti anamugwira ku Gati.+

56 Ndikomereni mtima inu Mulungu, chifukwa anthu akundiukira.*

Tsiku lonse amamenyana nane ndi kundipondereza.

 2 Tsiku lonse adani anga amafuna kundiwakha ndi pakamwa pawo.

Anthu ambiri akumenyana nane modzikuza.

 3 Ndikamachita mantha,+ ndimadalira inu.+

 4 Ndimadalira Mulungu, ndimamutamanda chifukwa cha mawu ake.

Ine ndimadalira Mulungu, sindikuopa.

Kodi munthu wamba angandichite chiyani?+

 5 Tsiku lonse amasokoneza zolinga zanga.

Nthawi zonse amaganiza zondivulaza.+

 6 Iwo amandibisalira kuti andiukire,

Nthawi zonse amaonetsetsa mmene ndikuyendera,+

Pofuna kuchotsa moyo wanga.+

 7 Alangeni chifukwa cha zochita zawo zoipa.

Inu Mulungu, gwetsani mitundu ya anthu mutakwiya.+

 8 Inu mukudziwa bwino za kuthawathawa kwanga.+

Sungani misozi yanga mʼthumba lanu lachikopa.+

Kodi misozi yanga sinalembedwe mʼbuku lanu?+

 9 Pa tsiku limene ndidzapemphe kuti mundithandize, adani anga adzathawa.+

Mulungu ali kumbali yanga. Sindikukaikira zimenezi.+

10 Ndimadalira Mulungu, ndimamutamanda chifukwa cha mawu ake.

Ndimadalira Yehova, ndimamutamanda chifukwa cha mawu ake.

11 Ine ndimadalira Mulungu. Sindikuopa.+

Kodi munthu wamba angandichite chiyani?+

12 Inu Mulungu, ine ndikuyenera kukwaniritsa zimene ndinakulonjezani.+

Ndidzapereka kwa inu nsembe zoyamikira.+

13 Chifukwa inu mwandipulumutsa* ku imfa.+

Ndipo mwateteza phazi langa kuti lisapunthwe,+

Kuti ndiyende pamaso pa Mulungu mʼkuwala kumene kumaunikira anthu amoyo.+

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimboyi iimbidwe motsatira kaimbidwe ka nyimbo yakuti “Musandiwononge.” Salimo la Davide. Mikitamu.* Pa nthawi imene anathawa Sauli nʼkukalowa mʼphanga.+

57 Ndikomereni mtima inu Mulungu, ndikomereni mtima,

Chifukwa ine ndathawira kwa inu.+

Ndathawira mumthunzi wa mapiko anu mpaka mavuto atadutsa.+

 2 Ndikufuulira Mulungu Wamʼmwambamwamba,

Mulungu woona amene akuthetsa mavuto amenewa kuti zinthu zindiyendere bwino.

 3 Adzatumiza thandizo kuchokera kumwamba nʼkundipulumutsa.+

Adzasokoneza wofuna kundiwakha ndi pakamwa pake. (Selah)

Mulungu adzasonyeza chikondi chake chokhulupirika ndi choonadi chake.+

 4 Ndazunguliridwa ndi mikango.+

Ndikuyenera kugona pakati pa anthu amene ali ngati nyama zoopsa zodya anthu,

Amene mano awo ali ngati mikondo ndi mivi,

Ndipo lilime lawo lili ngati lupanga lakuthwa.+

 5 Inu Mulungu, kwezekani kupitirira kumwamba.

Ulemerero wanu ukhale padziko lonse lapansi.+

 6 Iwo atchera ukonde kuti akole mapazi anga.+

Ndili ndi nkhawa yaikulu.+

Anakumba dzenje panjira yanga,

Koma agweramo okha.+ (Selah)

 7 Ndatsimikiza mtima, Inu Mulungu,+

Ndatsimikiza mtima.

Ndidzakuimbirani nyimbo ndi zipangizo zoimbira.

 8 Dzuka, iwe ulemerero wanga.

Dzuka, iwe choimbira cha zingwe, ndi iwenso zeze.

Ine ndidzadzuka mʼbandakucha.+

 9 Ndidzakutamandani pakati pa mitundu ya anthu, inu Yehova.+

Ndidzaimba nyimbo zokutamandani pakati pa mitundu ya anthu.+

10 Chifukwa chikondi chanu chokhulupirika nʼchachikulu moti chafika kumwamba,+

Ndipo kukhulupirika kwanu kwafika kuthambo.

11 Inu Mulungu, kwezekani kupitirira kumwamba.

Ulemerero wanu ukhale padziko lonse lapansi.+

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimboyi iimbidwe motsatira kaimbidwe ka nyimbo yakuti “Musandiwononge.” Salimo la Davide. Mikitamu.*

58 Kodi mungalankhule bwanji za chilungamo mutakhala chete?+

Kodi mungaweruze mwachilungamo, inu ana a anthu?+

 2 Ayi, mʼmalomwake mukuganiza zochita zinthu zopanda chilungamo mumtima mwanu,+

Ndipo mumalimbikitsa zachiwawa mʼdzikoli.+

 3 Oipa amasochera* akangobadwa.*

Iwo amakhala osamvera komanso abodza kuchokera nthawi imene anabadwa.

 4 Iwo ali ndi poizoni ngati wa njoka.+

Ndipo ndi ogontha ngati njoka ya mamba imene yatseka makutu ake.

 5 Singamve mawu a anthu amatsenga,

Ngakhale atachita matsengawo mwaluso.

 6 Inu Mulungu, agululeni mano mʼkamwa mwawo.

Inu Yehova, thyolani nsagwada za mikango* imeneyi.

 7 Asowe ngati madzi amene akuyenda.

Mulungu akoke uta wake nʼkuwagwetsa ndi mivi yake.

 8 Akhale ngati nkhono imene imasungunuka ikamayenda.

Ngati mwana wa mayi amene wapita padera, yemwe saona dzuwa.

 9 Miphika yanu isanayambe kumva kutentha kwa moto wa mitengo yaminga,

Mulungu adzauluza mitengo yaiwisi komanso imene ikuyaka ngati ikuuluzika ndi mphepo yamkuntho.+

10 Wolungama adzasangalala chifukwa chakuti waona oipa akupatsidwa chilango.+

Mapazi ake adzaponda magazi a anthu oipa.+

11 Kenako anthu adzati: “Ndithudi wolungama amalandira mphoto.+

Ndithudi pali Mulungu amene amaweruza padziko lapansi.”+

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimboyi iimbidwe motsatira kaimbidwe ka nyimbo yakuti “Musandiwononge.” Salimo la Davide. Mikitamu.* Pa nthawi imene Sauli anatumiza anthu kukadikirira nyumba yake kuti amuphe.+

59 Inu Mulungu wanga, ndipulumutseni kwa adani anga.+

Nditetezeni kwa anthu amene akundiukira.+

 2 Ndilanditseni kwa anthu ochita zoipa,

Ndipo ndipulumutseni kwa anthu achiwawa.*

 3 Inu Yehova, taonani! Iwo amandidikirira panjira.+

Anthu amphamvu amandiukira

Koma osati chifukwa chakuti ndapanduka kapena kuchita tchimo lililonse.+

 4 Ngakhale kuti sindinalakwe chilichonse, iwo akuthamanga ndipo akukonzekera kundiukira.

Nyamukani pamene ine ndikuitana kuti muone zimene zikundichitikira.

 5 Chifukwa inu Yehova, Mulungu wa magulu ankhondo akumwamba, ndinu Mulungu wa Isiraeli.+

Nyamukani ndipo muone zimene mitundu yonse ya anthu ikuchita.

Musasonyeze chifundo kwa aliyense woipa komanso wachiwembu.+ (Selah)

 6 Amabwera madzulo aliwonse.+

Amauwa ngati agalu+ ndipo amazungulira mzinda wonse.+

 7 Tamverani zimene zikutuluka pakamwa pawo.

Milomo yawo ili ngati malupanga,+

Chifukwa iwo akuti: “Ndani akumvetsera?”+

 8 Koma inu Yehova, mudzawaseka.+

Mudzanyoza mitundu yonse ya anthu.+

 9 Inu Mphamvu yanga, ndidzayangʼanabe kwa inu.+

Chifukwa Mulungu ndi malo anga othawirako otetezeka.*+

10 Mulungu amene amandisonyeza chikondi chokhulupirika adzandithandiza.+

Mulungu adzachititsa kuti ndione adani anga atagonja.+

11 Musawaphe, kuti anthu a mtundu wanga asaiwale.

Ndi mphamvu zanu achititseni kuti aziyendayenda,

Achititseni kuti agwe, inu Yehova, chishango chathu.+

12 Chifukwa cha tchimo lapakamwa pawo ndi mawu a milomo yawo,

Ndiponso chifukwa cha mawu otukwana komanso achinyengo amene amalankhula,+

Akodwe ndi kunyada kwawoko.

13 Muwawononge onse mutakwiya.+

Muwawononge kuti asakhaleponso.

Muwadziwitse kuti Mulungu akulamulira mbadwa za Yakobo mpaka kumalekezero a dziko lapansi.+ (Selah)

14 Asiyeni abwerenso madzulo.

Asiyeni auwe ngati agalu ndipo azizungulira mzinda wonse.+

15 Asiyeni aziyendayenda kufunafuna chakudya.+

Musalole kuti akhute kapena kupeza malo ogona.

16 Koma ine, ndidzaimba za mphamvu zanu.+

Mʼmawa ndidzanena mosangalala za chikondi chanu chokhulupirika.

Chifukwa inu ndinu malo anga othawirako otetezeka,+

Ndiponso malo anga othawirako pa nthawi ya mavuto.+

17 Inu Mphamvu yanga, ndidzakuimbirani nyimbo zokutamandani,+

Chifukwa Mulungu ndi malo anga othawirako otetezeka, Mulungu amene amandisonyeza chikondi chokhulupirika.+

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimboyi iimbidwe motsatira kaimbidwe ka nyimbo ya “Duwa la Chikumbutso.” Mikitamu.* Salimo la Davide. Nyimbo yophunzitsira. Pa nthawi imene Davide anali pankhondo ndi Aramu-naharaimu ndi Aramu-Zoba, ndipo Yowabu anabwerera nʼkukapha Aedomu 12,000 mʼchigwa cha Mchere.+

60 Inu Mulungu, munatikana ndipo munatigonjetsa.+

Munatikwiyira. Koma tsopano tiloleni tibwerere kwa inu.

 2 Mwachititsa kuti dziko lapansi ligwedezeke ndipo mwalingʼamba.

Tsekani mingʼalu yake, chifukwa likugwa.

 3 Mwachititsa kuti anthu anu akumane ndi mavuto.

Mwatimwetsa vinyo amene wachititsa kuti tiziyenda dzandidzandi.+

 4 Perekani* chizindikiro kwa anthu amene amakuopani

Kuti athawe ndi kuzemba uta. (Selah)

 5 Kuti anthu amene mumawakonda apulumutsidwe,

Tipulumutseni ndi dzanja lanu lamanja ndipo mutiyankhe.+

 6 Popeza ndi woyera,* Mulungu walankhula kuti:

“Ndidzasangalala popereka Sekemu ngati cholowa,+

Ndipo ndidzayezera anthu anga malo mʼchigwa cha Sukoti.+

 7 Giliyadi ndi wanga, ngati mmene zilili ndi Manase,+

Ndipo Efuraimu ndi chipewa choteteza* mutu wanga.

Yuda akuimira mphamvu zanga zolamula.+

 8 Mowabu ndi beseni langa losambiramo.+

Edomu ndidzamuponyera nsapato zanga.+

Ndidzafuula mosangalala chifukwa chogonjetsa Filisitiya.”+

 9 Ndi ndani amene adzandibweretse kumzinda wozunguliridwa ndi adani?*

Ndi ndani amene adzanditsogolere mpaka kukafika ku Edomu?+

10 Kodi si inu Mulungu amene munatikana,

Mulungu wathu, amene simukutsogoleranso magulu athu ankhondo?+

11 Tithandizeni pamene tikukumana ndi mavuto,

Chifukwa chipulumutso chochokera kwa munthu nʼchopanda pake.+

12 Mulungu adzatipatsa mphamvu,+

Ndipo adzapondaponda adani athu.+

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimboyi iimbidwe ndi zoimbira za zingwe. Salimo la Davide.

61 Inu Mulungu, imvani kulira kwanga kopempha thandizo.

Mvetserani pemphero langa mwatcheru.+

 2 Kuchokera kumalekezero a dziko lapansi ndidzafuulira inu

Pamene mtima wanga walefuka.*+

Nditsogolereni nʼkundikweza pathanthwe lalitali kuposa msinkhu wanga.+

 3 Chifukwa inu ndinu malo anga othawirako,

Nsanja yolimba imene imanditeteza kwa mdani.+

 4 Ndidzakhala mlendo mutenti yanu mpaka kalekale.+

Ndidzabisala mumthunzi wa mapiko anu.+ (Selah)

 5 Chifukwa inu Mulungu, mwamva malonjezo anga.

Mwandipatsa cholowa chimene ndi cha anthu amene amaopa dzina lanu.+

 6 Mudzatalikitsa moyo wa mfumu,*+

Ndipo idzakhala ndi moyo ku mibadwomibadwo.

 7 Mfumuyo idzakhala pampando wachifumu mpaka kalekale pamaso pa Mulungu.+

Chikondi chanu chokhulupirika komanso kukhulupirika kwanu ziiteteze.+

 8 Mukatero ndidzaimba nyimbo zotamanda dzina lanu mpaka kalekale,+

Pamene ndikukwaniritsa malonjezo anga tsiku ndi tsiku.+

Kwa wotsogolera nyimbo. Aimbe nyimboyi pa Yedutuni.* Nyimbo ya Davide.

62 Ndithudi, ndikuyembekezera* Mulungu modekha.

Chipulumutso changa chimachokera kwa iye.+

 2 Iye ndi thanthwe langa komanso ndi amene amandipulumutsa, malo anga othawirako otetezeka.*+

Sindidzagwedezeka kwambiri.+

 3 Kodi mudzamenya munthu kuti mumuphe mpaka liti?+

Nonsenu ndinu oopsa ngati khoma lopendekeka, khoma lamiyala limene latsala pangʼono kugwa.

 4 Iwo amakambirana kuti amuchotse pa udindo wake wapamwamba.*

Bodza limawasangalatsa.

Iwo amadalitsa ndi pakamwa pawo, koma mumtima mwawo amakhala akutemberera.+ (Selah)

 5 Ndithudi, ndikuyembekezera Mulungu modekha*+

Chifukwa chiyembekezo changa chimachokera kwa iye.+

 6 Ndithudi, iye ndi thanthwe langa komanso amene amandipulumutsa, malo anga othawirako otetezeka.

Sindidzagwedezeka.+

 7 Chipulumutso ndi ulemerero wanga zimachokera kwa Mulungu.

Mulungu ndi thanthwe langa lolimba ndi malo anga othawirako.+

 8 Muzimudalira nthawi zonse, anthu inu.

Mukhuthulireni zonse zamumtima mwanu.+

Mulungu ndi malo athu othawirako.+ (Selah)

 9 Ana a anthu ali ngati mpweya,

Ana a anthu ndi malo othawirako osadalirika.+

Onse pamodzi akaikidwa pasikelo amapepuka kuposa mpweya.+

10 Musadalire chizolowezi chobera ena mwachinyengo,

Kapena kudalira uchifwamba.

Ngati chuma chanu chachuluka, mtima wanu usakhale pachumacho.+

11 Kawiri konse ndamva Mulungu akunena kuti:

Mphamvu ndi za Mulungu.+

12 Komanso chikondi chokhulupirika ndi chanu, inu Yehova,+

Chifukwa inu mumabwezera aliyense mogwirizana ndi zochita zake.+

Nyimbo ya Davide, pamene anali mʼchipululu cha Yuda.+

63 Inu Mulungu, ndinu Mulungu wanga, ine ndikukufunafunani.+

Ine ndikulakalaka inu.*+

Ndalefuka* chifukwa cholakalaka inu

Mʼdziko louma komanso lopanda madzi, kumene sikumera chilichonse.+

 2 Choncho ndakuonani mʼmalo oyera.

Ndaona mphamvu zanu ndi ulemerero wanu.+

 3 Chifukwa chikondi chanu chokhulupirika nʼchabwino kuposa moyo,+

Milomo yanga idzakulemekezani.+

 4 Choncho ndidzakutamandani moyo wanga wonse.

Ndidzapemphera mʼdzina lanu nditakweza manja anga.

 5 Ndakhutira* ndi gawo labwino komanso losangalatsa kwambiri,*

Choncho milomo yanga idzakutamandani pofuula mosangalala.+

 6 Ndimakukumbukirani ndili pabedi langa,

Ndimaganizira mozama za inu usiku wonse.*+

 7 Chifukwa inu mumandithandiza,+

Ndipo ndimafuula mosangalala mumthunzi wa mapiko anu.+

 8 Ndimakhala* nanu pafupi kwambiri.

Dzanja lanu lamanja limandigwira mwamphamvu.+

 9 Koma amene akufuna kuwononga moyo wanga*

Adzatsikira kumanda.

10 Adzaphedwa ndi lupanga,

Adzakhala chakudya cha nkhandwe.

11 Koma mfumu idzasangalala ndi zimene Mulungu adzaichitire.

Munthu aliyense wolumbira mʼdzina la Mulungu adzasangalala kwambiri,*

Chifukwa pakamwa pa anthu olankhula zabodza padzatsekedwa.

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ya Davide.

64 Inu Mulungu, imvani mawu anga pamene ndikukuchondererani.+

Tetezani moyo wanga ku zinthu zoopsa zimene mdani akuchita.

 2 Ndibiseni ku ziwembu zachinsinsi za anthu oipa,+

Kwa gulu la anthu ochita zoipa.

 3 Iwo amanola lilime lawo ngati lupanga.

Amakonzekera kuponya mawu awo opweteka ngati mivi,

 4 Kuti alase munthu wosalakwa atamubisalira.

Amamulasa modzidzimutsa ndiponso mopanda mantha.

 5 Amaumirira kuti akwaniritse zolinga zawo zoipa,*

Amakambirana zimene angachite kuti abise misampha yawo.

Iwo amanena kuti: “Angaione ndani?”+

 6 Amafufuza njira zatsopano zochitira zinthu zoipa.

Mwachinsinsi amakonza njira zochitira ziwembu zawo mochenjera.+

Zimene munthu aliyense akuganiza mumtima mwake, nʼzovuta kuzimvetsa.

 7 Koma Mulungu adzawalasa ndi muvi.+

Adzavulazidwa ndi muvi modzidzimutsa.

 8 Adzawonongedwa chifukwa cha zolankhula za lilime lawo lomwe,+

Onse amene adzaone zimenezi adzapukusa mitu yawo.

 9 Ndiyeno anthu onse adzachita mantha,

Ndipo adzalengeza zimene Mulungu wachita,

Iwo adzamvetsa bwino zimene iye amachita.+

10 Wolungama adzasangalala chifukwa cha Yehova ndipo adzathawira kwa iye.+

Onse owongoka mtima adzasangalala kwambiri.*

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ndi Salimo la Davide.

65 Inu Mulungu, tidzakutamandani mu Ziyoni,+

Tidzakwaniritsa malonjezo athu kwa inu.+

 2 Inu Wakumva pemphero, anthu a mitundu yonse adzabwera kwa inu.+

 3 Zolakwa zanga zandikulira,+

Koma inu mumatikhululukira machimo athu.+

 4 Wosangalala ndi munthu amene inu mwamusankha nʼkumubweretsa pafupi ndi inu,

Kuti akhale mʼmabwalo anu.+

Tidzakhutira ndi zinthu zabwino zamʼnyumba yanu,+

Kachisi wanu woyera.*+

 5 Mudzatiyankha pochita zinthu zachilungamo zomwe ndi zochititsa mantha,+

Inu Mulungu amene mumatipulumutsa.

Anthu amene amakhala kumbali zonse za dziko lapansi amakudalirani+

Kuphatikizapo amene amakhala kutali, kutsidya la nyanja.

 6 Ndi mphamvu zanu, munakhazikitsa mapiri mʼmalo ake,

Inu muli ndi mphamvu zochuluka.+

 7 Mumachititsa kuti nyanja imene ikuchita mafunde ikhale bata.+

Mumaletsa phokoso la mafunde ake komanso chipwirikiti cha mitundu ya anthu.+

 8 Anthu okhala mʼmadera akutali adzachita mantha ndi zizindikiro zanu.+

Mudzachititsa kuti anthu amene amakhala kumene dzuwa limatulukira mpaka kumene limalowera afuule mosangalala.

 9 Inu mumasamalira dziko lapansi,

Mumalichititsa kuti libale zipatso zambiri* komanso kuti likhale lachonde.+

Mtsinje wochokera kwa Mulungu ndi wodzadza ndi madzi.

Mumachititsa kuti dziko lapansi lipereke chakudya kwa anthu,+

Umu ndi mmene dziko lapansi munalipangira.

10 Mumanyowetsa minda yake komanso kusalaza dothi limene lalimidwa,*

Mumaifewetsa ndi mvula yamvumbi. Mumadalitsa zomera zake.+

11 Chaka mumachiveka zinthu zabwino ndipo zimakhala ngati mwachiveka chisoti chachifumu.

Munjira zanu mumakhala zinthu zambiri zabwino.*+

12 Mʼmalo odyetserako ziweto amʼchipululu muli msipu wambiri.*+

Ndipo zitunda zavekedwa chisangalalo.+

13 Malo odyetserako ziweto adzaza ndi nkhosa,

Ndipo mʼzigwa muli tirigu yekhayekha.+

Malo onsewa akufuula komanso kuimba mosangalala.+

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ndi Salimo.

66 Dziko lonse lapansi lifuule mosangalala ndipo litamande Mulungu.+

 2 Imbani nyimbo zotamanda dzina lake laulemerero.

Mʼpatseni ulemerero ndipo mumutamande.+

 3 Muuzeni Mulungu kuti: “Ntchito zanu ndi zochititsadi mantha!+

Chifukwa cha mphamvu zanu zazikulu,

Adani anu adzabwera kwa inu mwamantha.+

 4 Anthu onse padziko lapansi adzakugwadirani.+

Adzaimba nyimbo zokutamandani,

Adzaimba nyimbo zotamanda dzina lanu.”+ (Selah)

 5 Bwerani mudzaone ntchito za Mulungu.

Zimene wachitira ana a anthu ndi zochititsa mantha.+

 6 Anasandutsa nyanja kukhala malo ouma,+

Anthu anawoloka mtsinje poyenda ndi mapazi awo.+

Pamenepo tinasangalala chifukwa cha zimene Mulungu anatichitira.+

 7 Iye akulamulira ndi mphamvu zake mpaka kalekale.+

Maso ake akuyangʼanitsitsa mitundu ya anthu.+

Anthu osamvera asadzikweze.+ (Selah)

 8 Tamandani Mulungu wathu, inu mitundu ya anthu,+

Mutamandeni mofuula.

 9 Iye amatithandiza kuti tikhalebe ndi moyo,+

Salola kuti mapazi athu apunthwe.*+

10 Chifukwa inu Mulungu mwatifufuza.+

Mwatiyenga ngati mmene amayengera siliva.

11 Mwatikola ndi ukonde wanu wosakira nyama,

Mwatisenzetsa katundu wolemera kwambiri.*

12 Munalola kuti munthu wamba atipondeponde.*

Tinadutsa pamoto ndi pamadzi,

Kenako munatibweretsa pamalo ampumulo.

13 Ndidzalowa mʼnyumba yanu ndi nsembe zopsereza zathunthu.+

Ine ndidzakwaniritsa malonjezo anga kwa inu+

14 Amene milomo yanga inalonjeza,+

Ndiponso amene pakamwa panga pananena pa nthawi imene ndinali pamavuto aakulu.

15 Ndidzapereka kwa inu nsembe zopsereza za nyama zonenepa,

Ndidzapereka nsembe nkhosa zamphongo.

Ndidzapereka ngʼombe zamphongo pamodzi ndi mbuzi zamphongo. (Selah)

16 Bwerani mudzamve, inu nonse amene mumaopa Mulungu,

Ndipo ine ndidzakuuzani zimene wandichitira.+

17 Ndinamuitana ndi pakamwa panga,

Ndipo ndinamutamanda ndi lilime langa.

18 Ngati mumtima mwanga ndikanakhala ndi maganizo aliwonse oti ndichitire munthu zoipa,

Yehova sakanandimvetsera.+

19 Koma Mulungu anamva.+

Anamvetsera pemphero langa mwatcheru.+

20 Atamandike Mulungu, amene sananyalanyaze pemphero langa

Kapena kulephera kundisonyeza chikondi chake chokhulupirika.

Kwa wotsogolera nyimbo: Nyimboyi iimbidwe ndi zipangizo za zingwe. Nyimbo ndi Salimo.

67 Mulungu adzatikomera mtima ndi kutidalitsa.

Iye adzasonyeza kuti akusangalala nafe+ (Selah)

 2 Kuti njira zanu zidziwike padziko lonse lapansi,+

Kuti mitundu yonse ya anthu idziwe kuti ndinu Mpulumutsi.+

 3 Inu Mulungu, mitundu ya anthu ikutamandeni,

Ndithu mitundu yonse ya anthu ikutamandeni.

 4 Mitundu ya anthu isangalale ndi kufuula mokondwera,+

Chifukwa inu mudzaweruza anthu mwachilungamo.+

Mudzatsogolera mitundu ya anthu padziko lapansi. (Selah)

 5 Inu Mulungu, mitundu ya anthu ikutamandeni,

Ndithu mitundu yonse ya anthu ikutamandeni.

 6 Dziko lapansi lidzapereka zipatso zake.+

Mulungu, ndithu Mulungu wathu, adzatidalitsa.+

 7 Mulungu adzatidalitsa,

Ndipo anthu onse apadziko lapansi adzamuopa.*+

Kwa wotsogolera nyimbo. Salimo ndi nyimbo ya Davide.

68 Mulungu anyamuke, adani ake amwazike,

Ndipo amene amadana naye athawe pamaso pake.+

 2 Mofanana ndi mphepo imene imathamangitsa utsi, inunso muwathamangitsire kutali.

Mofanana ndi phula limene limasungunuka pamoto,

Anthu oipa awonongeke pamaso pa Mulungu.+

 3 Koma olungama asangalale,+

Asangalale kwambiri pamaso pa Mulungu,

Adumphe ndi chisangalalo.

 4 Imbirani Mulungu, muimbireni nyimbo zotamanda dzina lake.+

Imbirani Iye amene akudutsa mʼchipululu.*

Dzina lake ndi Ya.*+ Sangalalani pamaso pake.

 5 Bambo wa ana amasiye komanso amene amateteza* akazi amasiye+

Ndi Mulungu amene amakhala mʼmalo ake oyera.+

 6 Anthu amene alibe wowathandiza, Mulungu amawapatsa nyumba kuti azikhalamo.+

Amamasula akaidi nʼkuwathandiza kuti zinthu ziwayendere bwino.+

Koma anthu osamvera* adzakhala mʼdziko louma.+

 7 Inu Mulungu, pamene munkatsogolera anthu anu,+

Pamene munkadutsa mʼchipululu, (Selah)

 8 Dziko lapansi linagwedezeka,+

Kumwamba kunagwa mvula chifukwa cha inu Mulungu,

Phiri la Sinai ili linagwedezeka chifukwa cha inu Mulungu, Mulungu wa Isiraeli.+

 9 Inu Mulungu, munagwetsa mvula yokwanira.

Munapatsa mphamvu anthu anu amene anali ofooka.*

10 Iwo ankakhala mʼmudzi wanu wamatenti.+

Inu Mulungu, chifukwa chakuti ndinu wabwino, munapereka zinthu zofunika kwa anthu osauka.

11 Yehova wapereka lamulo* kwa anthu ake,

Ndipo akazi amene akulengeza uthenga wabwino* ndi gulu lalikulu.+

12 Mafumu okhala ndi magulu a asilikali amathawa,+ ndithu amathawadi.

Mkazi amene amangokhala pakhomo, amalandira nawo zinthu zimene zalandidwa kunkhondo.+

13 Ngakhale anthu inu mutagona pambali pa moto mumsasa,

Mudzalandira njiwa imene mapiko ake ndi okutidwa ndi siliva,

Ndipo nthenga zakumapeto a mapiko ake ndi zagolide woyenga bwino.*

14 Pamene Wamphamvuyonse anamwaza mafumu amʼdzikomo,+

Mu Zalimoni munagwa sinowo.*

15 Phiri la ku Basana+ ndi phiri la Mulungu.*

Phiri la ku Basana ndi phiri lansonga zitalizitali.

16 Nʼchifukwa chiyani inu mapiri ansonga zitalizitali mumayangʼana mwansanje

Phiri limene Mulungu wasankha* kuti azikhalamo?+

Ndithudi, Yehova adzakhala mʼphiri limenelo mpaka kalekale.+

17 Magaleta ankhondo a Mulungu ali mʼmagulu a masauzande osawerengeka, ali mʼmagulu masauzandemasauzande.+

Yehova walowa mʼmalo oyera kuchokera kuphiri la Sinai.+

18 Munakwera pamalo apamwamba.+

Munatenga anthu ogwidwa ukapolo.

Munatenga amuna kuti akhale mphatso,+

Ndithu inu Ya,* Mulungu wathu, mwatenga ngakhale anthu osamvera+ kuti mukhale pakati pawo.

19 Atamandike Yehova, amene amanyamula katundu wathu tsiku ndi tsiku,+

Mulungu woona amene amatipulumutsa. (Selah)

20 Mulungu woona ndi Mulungu amene amatipulumutsa.+

Ndipo Yehova Ambuye Wamkulu Koposa amatipulumutsa ku imfa.+

21 Ndithudi, Mulungu adzaphwanya mitu ya adani ake,

Adzaphwanya mutu wa aliyense amene akupitiriza* kuchita machimo.+

22 Yehova wanena kuti: “Ndidzawabweza kuchokera ku Basana,+

Ndidzawatulutsa mʼnyanja yakuya,

23 Kuti mapazi anu aponde magazi a adani anu,+

Ndiponso kuti malilime a agalu anu anyambite magazi a adani anu.”

24 Iwo aona magulu a anthu anu akuyendera pamodzi, inu Mulungu,

Magulu a anthu oyendera pamodzi a Mulungu wanga, Mfumu yanga, akulowa kumalo opatulika.+

25 Oimba nyimbo akuyenda patsogolo, oimba zoimbira za zingwe akuyenda pambuyo pawo,+

Pakati pali atsikana amene akuimba maseche.+

26 Pamisonkhano tamandani Mulungu,

Tamandani Yehova, inu nonse amene moyo wanu ukuchokera mu Kasupe wa Isiraeli.+

27 Pali fuko lalingʼono la Benjamini+ limene likugonjetsa anthu,

Pali akalonga a Yuda pamodzi ndi chigulu chawo chimene chikuchita phokoso,

Palinso akalonga a Zebuloni komanso akalonga a Nafitali.

28 Mulungu wanu waganiza kuti akupatseni mphamvu.

Sonyezani mphamvu zanu, Inu Mulungu, amene mumatithandiza.+

29 Chifukwa cha kachisi wanu yemwe ali ku Yerusalemu,+

Mafumu adzabweretsa mphatso kwa inu.+

30 Dzudzulani nyama zakutchire zimene zimakhala mʼmabango,

Gulu la ngʼombe zamphongo+ limodzi ndi ana awo,

Mpaka mitundu ya anthu itagwada nʼkubweretsa ndalama zasiliva.

Koma iye wabalalitsa mitundu ya anthu imene imasangalala ndi nkhondo.

31 Zinthu zopangidwa ndi kopa* zidzabwera kuchokera* ku Iguputo,+

Mwamsanga, dziko la Kusi lidzapereka mphatso kwa Mulungu.

32 Inu maufumu a dziko lapansi, imbirani Mulungu,+

Imbani nyimbo zotamanda Yehova, (Selah)

33 Imbirani iye amene wakwera pamwamba pa kumwamba,+ kumene kwakhalapo kuyambira kalekale.

Mawu ake amphamvu amamveka ngati bingu.

34 Vomerezani kuti Mulungu ndi wamphamvu zochuluka.+

Ulemerero wake uli pa Isiraeli,

Ndipo amasonyeza mphamvu zake kuchokera kumwamba.*

35 Mulungu walamula kuti anthu amuope komanso amupatse ulemu mʼmalo ake opatulika aulemerero.+

Iye ndi Mulungu wa Isiraeli,

Amene amapereka mphamvu ndi nyonga kwa anthu.+

Mulungu atamandike.

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimboyi iimbidwe motsatira kaimbidwe ka “Nyimbo ya Maluwa.” Salimo la Davide.

69 Ndipulumutseni, inu Mulungu, chifukwa madzi atsala pangʼono kutenga moyo wanga.+

 2 Ndamira mʼmatope akuya, mmene mulibe malo oponda.+

Ndalowa mʼmadzi akuya,

Ndipo mtsinje wa madzi othamanga wandikokolola.+

 3 Ndatopa ndi kuitana,+

Mawu anga asasa.

Maso anga achita mdima poyembekezera Mulungu wanga.+

 4 Anthu amene amadana nane popanda chifukwa+

Ndi ambiri kuposa tsitsi lamʼmutu mwanga.

Amene akufuna kuchotsa moyo wanga,

Adani anga,* omwe ndi anthu achinyengo, achuluka kwambiri.

Anandikakamiza kuti ndibweze zinthu zimene sindinabe.

 5 Inu Mulungu, mukudziwa kupusa kwanga,

Ndipo zolakwa zanga sizinabisike kwa inu.

 6 Anthu onse amene akuyembekezera inu asachite manyazi chifukwa cha ine,

Inu Ambuye Wamkulu Koposa, Yehova wa magulu ankhondo akumwamba.

Anthu amene akufunafuna inu, asachite manyazi chifukwa cha ine,

Inu Mulungu wa Isiraeli.

 7 Ine ndanyozedwa chifukwa cha inu,+

Manyazi aphimba nkhope yanga.+

 8 Ndakhala mlendo kwa abale anga,

Ndakhala mlendo pakati pa ana aamuna a mayi anga.+

 9 Kudzipereka kwanga panyumba yanu kuli ngati moto umene ukuyaka mumtima mwanga,+

Ndipo chipongwe cha anthu amene amakunyozani chandigwera.+

10 Nditasonyeza kudzichepetsa posala kudya,*

Anthu anandinyoza chifukwa cha zimenezo.

11 Pamene ndinavala ziguduli,

Iwo anayamba kundinyoza.*

12 Anthu amene amakhala pageti la mzinda amandinena,

Ndipo anthu oledzera amanena za ine akamaimba nyimbo zawo.

13 Ndidzapemphera kwa inu Yehova,

Pa nthawi yovomerezeka kwa inu.+

Chifukwa cha chikondi chanu chokhulupirika chomwe ndi chochuluka, inu Mulungu,

Ndiyankheni ndipo musonyeze kuti ndinu Mpulumutsi wanga wodalirika.+

14 Ndipulumutseni mʼmatope

Musalole kuti ndimire.

Ndipulumutseni kwa anthu amene amadana nane

Ndiponso ku madzi akuya.+

15 Musalole kuti madzi osefukira andikokolole,+

Kapena kuti ndimire mʼmadzi akuya,

Kapenanso kuti dzenje* lindimeze nʼkutseka pakamwa pake.+

16 Ndiyankheni inu Yehova, chifukwa chikondi chanu chokhulupirika ndi chabwino.+

Maso anu akhale pa ine, mogwirizana ndi chifundo chanu chomwe ndi chochuluka,+

17 Ndipo musabise nkhope yanu kwa mtumiki wanu.+

Ndiyankheni mwamsanga, chifukwa ndili pamavuto aakulu.+

18 Bwerani pafupi ndi ine ndipo mundipulumutse.

Ndipulumutseni* kwa adani anga.

19 Inu mukudziwa mmene andinyozera, chipongwe chimene andichitira komanso mmene andichititsira manyazi.+

Adani anga onse mukuwaona.

20 Mtima wanga wasweka chifukwa cha kunyozedwa, ndipo bala lake ndi losachiritsika.*

Ndimayembekezera kuti wina andimvera chisoni, koma panalibe ndi mmodzi yemwe,+

Ndimayembekezera kuti wina anditonthoza, koma sanapezeke ngakhale mmodzi.+

21 Koma mʼmalo mwa chakudya anandipatsa poizoni,*+

Ndipo pamene ndinali ndi ludzu anandipatsa vinyo wosasa kuti ndimwe.+

22 Tebulo lawo likhale msampha kwa iwo,

Ndipo zinthu zimene zikuwayendera bwino zikhale ngati khwekhwe kwa iwo.+

23 Maso awo achite mdima kuti asaone,

Ndipo chititsani miyendo yawo kuti izinjenjemera* nthawi zonse.

24 Akhuthulireni ukali wanu,

Ndipo mkwiyo wanu woyaka moto uwagwere.+

25 Msasa wawo* ukhale bwinja,

Ndipo mʼmatenti awo musapezeke munthu wokhalamo.+

26 Chifukwa iwo amalondalonda munthu amene inu mwamulanga,

Ndipo amakamba miseche ya ululu wa anthu amene inu mwawavulaza.

27 Muwapatse chilango champhamvu chifukwa cha zolakwa zawo,

Ndipo asapindule ndi chilungamo chanu.

28 Mayina awo afufutidwe mʼbuku la anthu amoyo,*+

Ndipo iwo asalembedwe mʼbuku limene muli mayina a anthu olungama.+

29 Koma ine ndavutika ndipo ndikumva ululu.+

Inu Mulungu, mundipulumutse komanso munditeteze.

30 Ndidzaimba nyimbo zotamanda dzina la Mulungu,

Ndipo ndidzamulemekeza komanso kumuyamikira.

31 Zimenezi zidzasangalatsa kwambiri Yehova kuposa ngʼombe yamphongo,

Kuposa ngʼombe yamphongo yaingʼono imene ili ndi nyanga komanso ziboda.+

32 Anthu ofatsa adzaona zimenezi ndipo adzasangalala.

Inu amene mukutumikira Mulungu, mitima yanu ipezenso mphamvu.

33 Chifukwa Yehova akumvetsera osauka,+

Ndipo sadzanyoza anthu ake amene agwidwa ukapolo.+

34 Kumwamba ndi dziko lapansi zimutamande,+

Chimodzimodzinso nyanja ndi chilichonse choyenda mmenemo.

35 Chifukwa Mulungu adzapulumutsa Ziyoni,+

Ndipo adzamanganso mizinda ya Yuda,

Iwo adzakhala mmenemo nʼkulitenga* kuti likhale lawo.

36 Mbadwa za atumiki ake zidzatenga dzikolo kuti likhale cholowa chawo,+

Ndipo anthu amene amakonda dzina lake+ adzakhala mmenemo.

Kwa wotsogolera nyimbo. Salimo la Davide. Nyimbo ya chikumbutso.

70 Inu Mulungu, ndipulumutseni,

Inu Yehova, ndithandizeni mofulumira.+

 2 Amene akufuna kuchotsa moyo wanga

Achititsidwe manyazi komanso anyozeke.

Amene akusangalala ndi tsoka langa

Abwerere mwamanyazi.

 3 Onse amene akunena kuti: “Eyaa! Eyaa!”

Abwezedwe mwamanyazi.

 4 Koma amene akufunafuna inu,

Akondwere ndi kusangalala chifukwa choti akudziwani.+

Amene amasangalala ndi njira imene mumapulumutsira anthu, nthawi zonse azinena kuti:

“Mulungu alemekezeke.”

 5 Koma ine ndine munthu wovutika komanso wosauka.+

Inu Mulungu, ndithandizeni mwamsanga.+

Inu ndi amene mumandithandiza komanso kundipulumutsa.+

Inu Yehova musachedwe.+

71 Inu Yehova, ine ndathawira kwa inu.

Musalole kuti ndichite manyazi.+

 2 Mundilanditse ndi kundipulumutsa chifukwa ndinu wolungama.

Tcherani khutu lanu* kwa ine nʼkundipulumutsa.+

 3 Mukhale thanthwe langa lachitetezo

Loti ndizilowamo nthawi zonse.

Lamulani kuti ndipulumutsidwe,

Chifukwa inu ndinu thanthwe langa ndi malo anga achitetezo.+

 4 Inu Mulungu wanga, ndipulumutseni mʼmanja mwa woipa,+

Kuti ndisagwidwe ndi munthu wochita zinthu mopondereza komanso wopanda chilungamo.

 5 Chifukwa chiyembekezo changa ndi inu Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.

Ndakhala ndikudalira inu kuyambira ndili mnyamata.+

 6 Ndakhala ndikudalira inu kuchokera tsiku limene ndinabadwa.

Inu ndi amene munanditulutsa mʼmimba mwa mayi anga.+

Ndimakutamandani nthawi zonse.

 7 Ndakhala ngati chinthu chodabwitsa kwa anthu ambiri,

Koma inu ndinu malo anga othawirako olimba.

 8 Mʼkamwa mwanga mwadzaza mawu otamanda inu.+

Tsiku lonse ndimanena za ulemerero wanu.

 9 Musanditaye pa nthawi imene ndakalamba.+

Musandisiye pa nthawi imene mphamvu zanga zatha.+

10 Adani anga amandinenera zoipa,

Ndipo anthu amene akufuna kuchotsa moyo wanga, amandikonzera chiwembu,+

11 Iwo akunena kuti: “Mulungu wamusiya.

Muthamangitseni nʼkumugwira chifukwa palibe womupulumutsa.”+

12 Inu Mulungu, musakhale kutali ndi ine.

Inu Mulungu wanga, ndithandizeni mofulumira.+

13 Anthu amene akudana nane

Achititsidwe manyazi ndipo awonongedwe.+

Amene akufuna nditakumana ndi tsoka

Agwidwe manyazi ndipo anyozeke.+

14 Koma ine ndipitiriza kuyembekezera.

Ndidzakutamandani mowirikiza kuposa kale.

15 Pakamwa panga padzanena za chilungamo chanu,+

Tsiku lonse padzanena za ntchito za chipulumutso chanu,

Ngakhale kuti nʼzochuluka ndipo sindingathe kuzimvetsa.*+

16 Ndidzabwera nʼkudzanena za zinthu zamphamvu zimene mumachita,

Inu Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.

Ndidzanena za chilungamo chanu chokha basi.

17 Inu Mulungu, mwandiphunzitsa kuyambira ndili mnyamata,+

Ndipo mpaka pano ndikupitiriza kulengeza ntchito zanu zodabwitsa.+

18 Ngakhale nditakalamba nʼkumera imvi, inu Mulungu musandisiye.+

Ndiloleni kuti ndiuze mʼbadwo wotsatira za mphamvu zanu*

Komanso za nyonga zanu kwa onse obwera mʼtsogolo.+

19 Chilungamo chanu, inu Mulungu chafika kumwamba.+

Mwachita zinthu zazikulu,

Inu Mulungu, ndi ndani angafanane nanu?+

20 Ngakhale kuti mwachititsa kuti ndikumane ndi mavuto komanso masoka ambiri,+

Bwezeretsani mphamvu zanga.

Nditulutseni mʼdzenje lakuya.*+

21 Chulukitsani ulemu wanga,

Ndipo mundizungulire ndi chitetezo chanu nʼkundilimbikitsa.

22 Mukatero, ndidzakutamandani ndi choimbira cha zingwe

Chifukwa cha kukhulupirika kwanu, inu Mulungu.+

Ndidzakuimbirani nyimbo zokutamandani ndi zeze,

Inu Woyera wa Isiraeli.

23 Pakamwa panga padzafuula mosangalala pamene ndikuimba nyimbo zokutamandani,+

Chifukwa mwapulumutsa moyo wanga.*+

24 Lilime langa lidzalankhula* za chilungamo chanu tsiku lonse,+

Chifukwa anthu amene akufuna kundiwononga adzachita manyazi ndiponso kunyozeka.+

Salimo lonena za Solomo.

72 Inu Mulungu, thandizani mfumu kuti iziweruza mogwirizana ndi zigamulo zanu,

Ndipo dziwitsani mwana wa mfumu za chilungamo chanu.+

 2 Ateteze anthu anu pa mlandu wawo pogwiritsa ntchito chilungamo,

Aweruze mwachilungamo milandu ya anthu anu onyozeka.+

 3 Mapiri abweretse mtendere kwa anthu,

Ndipo zitunda zibweretse chilungamo.

 4 Ateteze* anthu onyozeka pakati pa anthu,

Apulumutse ana a anthu osauka,

Ndipo aphwanye wobera anzake mwachinyengo.+

 5 Iwo adzakuopani kwa nthawi yonse imene dzuwa lidzakhalepo

Komanso kwa nthawi yonse imene mwezi udzakhalepo,

Adzakuopani ku mibadwomibadwo.+

 6 Adzakhala ngati mvula imene imagwera pa udzu umene watchetchedwa,

Ngati mvula yamvumbi imene imanyowetsa nthaka.+

 7 Mʼmasiku a ulamuliro wake, wolungama zinthu zidzamuyendera bwino,*+

Ndipo padzakhala mtendere wochuluka+ kwa nthawi yonse imene mwezi udzakhalepo.

 8 Iye adzakhala ndi anthu omugonjera* kuchokera kunyanja kukafika kunyanja,

Komanso kuchokera ku Mtsinje* kukafika kumalekezero a dziko lapansi.+

 9 Anthu amene amakhala mʼchipululu adzamugwadira,

Ndipo adani ake adzabwira fumbi.+

10 Mafumu a ku Tarisi komanso amʼzilumba adzapereka msonkho.+

Mafumu a ku Sheba ndi ku Seba adzapereka mphatso.+

11 Mafumu onse adzamugwadira,

Ndipo mitundu yonse ya anthu idzamutumikira.

12 Chifukwa adzapulumutsa wosauka amene akufuula popempha thandizo,

Komanso wonyozeka ndi aliyense amene alibe womuthandiza.

13 Adzamvera chisoni munthu wonyozeka ndi wosauka,

Ndipo adzapulumutsa miyoyo ya anthu osauka.

14 Adzawapulumutsa* kuti asaponderezedwe komanso kuchitiridwa zachiwawa,

Ndipo adzaona kuti magazi awo ndi amtengo wapatali.

15 Iye akhale ndi moyo wautali ndipo apatsidwe golide wa ku Sheba.+

Nthawi zonse anthu azimupempherera,

Ndipo azimudalitsa tsiku lililonse.

16 Padziko lapansi padzakhala tirigu wambiri.+

Pamwamba pa mapiri padzakhala tirigu wochuluka.

Zokolola za mfumu zidzachuluka ngati mitengo ya ku Lebanoni,+

Ndipo mʼmizinda, anthu adzaphuka ngati udzu wapanthaka.+

17 Dzina lake likhalebe mpaka kalekale,+

Ndipo lipitirize kutchuka kwa nthawi zonse pamene dzuwa lidzakhalepo.

Ndipo kudzera mwa iye, anthu apeze madalitso.+

Mitundu yonse ya anthu imutchule kuti ndi wosangalala.

18 Atamandike Yehova Mulungu, Mulungu wa Isiraeli,+

Iye yekha amene amachita zinthu zodabwitsa.+

19 Litamandike dzina lake laulemerero mpaka kalekale,+

Ndipo ulemerero wake udzaze dziko lonse lapansi.+

Ame! Ame!

20 Mapemphero a Davide mwana wa Jese, athera pamenepa.+

BUKU LACHITATU

(Masalimo 73-89)

Nyimbo ya Asafu.+

73 Mulungu ndi wabwinodi kwa Isiraeli, kwa anthu oyera mtima.+

 2 Koma ine mapazi anga anangotsala pangʼono kusochera,

Mapazi anga anangotsala pangʼono kuterereka.+

 3 Chifukwa ndinkachitira nsanje anthu onyada*

Ndikamaona mtendere wa anthu oipa.+

 4 Chifukwa samva ululu umene munthu amamva akamafa.

Matupi awo amakhala athanzi.*+

 5 Iwo savutika ngati mmene anthu ena amavutikira,+

Ndipo sakumana ndi mavuto mofanana ndi anthu ena.+

 6 Choncho kudzikuza kuli ngati mkanda mʼkhosi mwawo,+

Ndipo avala chiwawa ngati malaya.

 7 Maso awo akwiririka chifukwa cha kunenepa kwa nkhope yawo.*

Ali ndi zinthu zambiri kuposa zimene ankalakalaka mumtima mwawo.

 8 Iwo amanyodola komanso kulankhula zinthu zoipa.+

Amaopseza anthu monyada kuti awapondereza.+

 9 Amalankhula ngati kuti ali kumwamba,

Ndipo malilime awo akuyendayenda padziko lapansi mwamatama.

10 Choncho anthu a Mulungu amawatsatira,

Ndipo amamwa madzi awo omwe ndi ambiri.

11 Iwo amanena kuti: “Mulungu angadziwe bwanji?+

Kodi Wamʼmwambamwamba amadziwa chilichonse?”

12 Ndithudi, izi nʼzimene oipa amachita, amakhala mosatekeseka nthawi zonse.+

Iwo amawonjezera chuma chawo.+

13 Ndithudi, ndayeretsa mtima wanga pachabe,

Ndipo ndasamba mʼmanja mwanga pachabe posonyeza kuti ndine wosalakwa.+

14 Ndinkavutika tsiku lonse,+

Ndipo mʼmawa uliwonse ndinkadzudzulidwa.+

15 Koma ndikananena zinthu zimenezi,

Ndikanachitira chinyengo anthu anu.*

16 Nditayesa kuti ndimvetse zimenezi,

Zinali zopweteka kwa ine

17 Mpaka pamene ndinalowa mʼmalo opatulika aulemerero a Mulungu,

Ndipo ndinazindikira tsogolo lawo.

18 Ndithudi, mwawaika pamalo oterera.+

Mwawagwetsa kuti awonongeke.+

19 Iwo awonongedwa mwadzidzidzi.+

Afika pamapeto awo modzidzimutsa ndipo atha momvetsa chisoni!

20 Inu Yehova, mofanana ndi maloto amene amaiwalika munthu akadzuka,

Inunso mukadzuka mudzawakana.*

21 Koma mtima wanga unandipweteka,+

Ndipo mkati mwanga* ndinamva ululu.

22 Ndinali wopanda nzeru ndipo sindinkamvetsa zinthu.

Ndinali ngati nyama yosaganiza pamaso panu.

23 Koma tsopano ine ndili ndi inu nthawi zonse.

Mwandigwira dzanja langa lamanja.+

24 Mumanditsogolera ndi malangizo anu,+

Ndipo pambuyo pake mudzandipatsa ulemerero.+

25 Winanso ndi ndani kumwambako amene angandithandize?

Ndipo chifukwa chakuti inu muli ndi ine, palibenso chimene ndimalakalaka padziko lapansi.+

26 Thupi langa ndi mtima wanga zingalefuke,

Koma Mulungu ndi thanthwe la mtima wanga ndiponso cholowa changa mpaka kalekale.+

27 Ndithudi, anthu amene ali kutali ndi inu adzatheratu.

Mudzawononga* aliyense amene akukusiyani pochita chigololo.*+

28 Koma kwa ine, kuyandikira kwa Mulungu ndi chinthu chabwino.+

Ndapanga Yehova Ambuye Wamkulu Koposa kukhala malo anga othawirako,

Kuti ndilengeze za ntchito zanu zonse.+

Masikili.* Salimo la Asafu.+

74 Inu Mulungu, nʼchifukwa chiyani mwatikana mpaka kalekale?+

Nʼchifukwa chiyani mkwiyo wanu ukuyakira* nkhosa zimene mukuweta?+

 2 Kumbukirani anthu* amene munawatenga kalekale kuti akhale anu,+

Fuko limene munaliwombola kuti likhale cholowa chanu.+

Kumbukirani phiri la Ziyoni kumene inu mumakhala.+

 3 Pitani kumalo amene akhala owonongeka kuyambira kalekale.+

Mdani wawononga chilichonse mʼmalo opatulika.+

 4 Adani anu afuula mosangalala mʼmalo anu olambiriramo.*+

Aikamo mbendera zawo kuti zikhale zizindikiro.

 5 Anali ngati anthu amene akugwetsa mitengo ndi nkhwangwa mʼnkhalango yowirira.

 6 Anagumula zinthu zojambula mochita kugoba zamʼmakoma a malo opatulika+ ndi nkhwangwa komanso ndodo zachitsulo.

 7 Anawotcha malo anu opatulika.+

Anaipitsa chihema chokhala ndi dzina lanu nʼkuchigwetsera pansi.

 8 Iwo limodzi ndi ana awo ananena mumtima mwawo kuti:

“Malo onse amene anthu amalambirirako Mulungu mʼdzikoli, ayenera kutenthedwa.”

 9 Kulibe zizindikiro zathu zoti tizione.

Kulibenso mneneri wina aliyense amene watsala,

Ndipo pakati pathu palibe amene akudziwa kuti zimenezi zikhala chonchi kwa nthawi yayitali bwanji.

10 Inu Mulungu, kodi mdani adzapitiriza kunyoza mpaka liti?+

Kodi mdani adzachitira mwano dzina lanu mpaka kalekale?+

11 Nʼchifukwa chiyani mwabweza dzanja lanu, dzanja lanu lamanja?+

Lichotseni pachifuwa panu ndipo muwawononge.

12 Koma Mulungu ndi Mfumu yanga kuyambira kalekale,

Iye ndi amene amapulumutsa anthu padziko lapansi.+

13 Inu munavundula nyanja ndi mphamvu zanu.+

Munaphwanya mitu ya zilombo zamʼnyanja.

14 Inu munaphwanya mitu ya Leviyatani.*

Munamupereka kwa anthu kuti akhale chakudya kwa anthu amene amakhala mʼzipululu.

15 Inu munangʼamba nthaka nʼkupanga akasupe ndi mitsinje.+

Munaumitsa mitsinje imene inkakhala ndi madzi nthawi zonse.+

16 Masana ndi anu, usikunso ndi wanu.

Munapanga kuwala* komanso dzuwa.+

17 Munaika malire onse a dziko lapansi.+

Munapanga nyengo yachilimwe ndi nyengo yachisanu.+

18 Inu Yehova, kumbukirani mmene adani akunyozera,

Mmene anthu opusa akuchitira mwano dzina lanu.+

19 Musapereke moyo wa njiwa yanu kwa zilombo zakuthengo.

Musaiwale kwamuyaya moyo wa anthu anu ovutika.

20 Kumbukirani pangano lanu,

Chifukwa anthu achiwawa amabisalira anzawo mʼmalo amdima apadziko lapansi.

21 Musalole kuti munthu woponderezedwa abwerere mokhumudwa.+

Anthu onyozeka komanso osauka atamande dzina lanu.+

22 Nyamukani inu Mulungu, ndipo mudziteteze pa mlandu wanu.

Kumbukirani mmene munthu wopusa wakunyozerani tsiku lonse.+

23 Musaiwale zimene adani anu akunena.

Phokoso la anthu amene amakutsutsani likukwera kumwamba nthawi zonse.

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimboyi iimbidwe motsatira kaimbidwe ka nyimbo yakuti “Musandiwononge.” Nyimbo ndi Salimo la Asafu.+

75 Timakuyamikani, inu Mulungu, timakuyamikani.

Dzina lanu lili pafupi ndi ife,+

Ndipo anthu akulengeza ntchito zanu zodabwitsa.

 2 Inu mukuti: “Ndikasankha nthawi yoti ndiweruze,

Ndimaweruza mwachilungamo.

 3 Pamene dziko lapansi ndi onse okhala mmenemo ananjenjemera* ndi mantha,

Ine ndi amene ndinalimbitsa zipilala zake.” (Selah)

 4 Anthu odzitukumula ndinawauza kuti, “Musadzitukumule,”

Ndipo oipa ndinawauza kuti, “Musadzikuze chifukwa choti muli ndi mphamvu.*

 5 Musadzikuze chifukwa choti muli ndi mphamvu*

Kapena kulankhula mwamatama.

 6 Chifukwa ulemu wa munthu suchokera

Kumʼmawa, kumadzulo kapena kumʼmwera.

 7 Mulungu ndiye woweruza.+

Amatsitsa munthu wina nʼkukweza wina.+

 8 Mʼdzanja la Yehova muli kapu.+

Vinyo akuchita thovu ndipo wasakanizidwa bwino.

Ndithudi, iye adzakhuthula vinyo yense

Ndipo anthu onse oipa padziko lapansi adzamwa mpaka kugugudiza nsenga zake.”+

 9 Koma ine ndidzalengeza zimenezi mpaka kalekale.

Ndidzaimba nyimbo zotamanda Mulungu wa Yakobo.

10 Mulungu akuti: “Ndidzathetsa mphamvu* zonse za anthu oipa,

Koma ndidzachititsa kuti mphamvu* za anthu olungama zionekere bwino.”

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimboyi iimbidwe ndi zipangizo za zingwe. Nyimbo ndi Salimo la Asafu.+

76 Mulungu ndi wodziwika mu Yuda.+

Dzina lake ndi lalikulu mu Isiraeli.+

 2 Tenti yake ili ku Salemu,+

Malo ake okhala ali ku Ziyoni.+

 3 Kumeneko anathyola mivi yoyaka moto,

Anathyolanso chishango, lupanga ndi zida zankhondo.+ (Selah)

 4 Inu mumawala kwambiri.*

Ndinu waulemerero kuposa mapiri amene muli nyama zodya zinzake.

 5 Anthu olimba mtima alandidwa zinthu zawo.+

Iwo agona tulo,

Asilikali onse analibe mphamvu.+

 6 Chifukwa cha kudzudzula kwanu, inu Mulungu wa Yakobo,

Hatchi komanso wokwera galeta, onse agona tulo tofa nato.+

 7 Inu nokha ndinu wochititsa mantha.+

Ndi ndani angapirire mkwiyo wanu waukulu?+

 8 Munapereka chiweruzo muli kumwamba.+

Dziko lapansi linachita mantha ndipo linakhala chete+

 9 Pamene Mulungu ananyamuka kuti apereke chiweruzo,

Kuti apulumutse anthu onse ofatsa apadziko lapansi.+ (Selah)

10 Chifukwa mkwiyo wa munthu udzachititsa kuti mutamandidwe.+

Mudzadzikongoletsa ndi mkwiyo wawo wotsala.

11 Chitani malonjezo anu kwa Yehova Mulungu wanu ndipo muwakwaniritse+

Anthu onse amene amuzungulira abweretse mphatso zawo mwamantha.+

12 Mulungu adzachititsa manyazi atsogoleri onyada.

Iye amachititsa kuti mafumu apadziko lapansi akhale ndi mantha.

Kwa wotsogolera nyimbo. Aimbe nyimboyi pa Yedutuni.* Nyimbo ndi Salimo la Asafu.+

77 Ndidzafuulira Mulungu,

Ndithu, ndidzafuulira Mulungu, ndipo iye adzandimvetsera.+

 2 Pa tsiku limene ndakumana ndi mavuto ndimafunafuna Yehova.+

Usiku ndimakweza manja anga kwa iye ndipo sindisiya.*

Palibe chimene chimanditonthoza.

 3 Ndikakumbukira Mulungu ndimabuula.+

Ndimavutika kwambiri mumtima ndipo mphamvu zanga zimatha.*+ (Selah)

 4 Mumatsegula zikope zanga.

Ndavutika mumtima, moti sindingathe kulankhula.

 5 Ndikuganizira masiku akale,+

Ndikuganizira zaka zakale kwambiri.

 6 Usiku ndimakumbukira nyimbo yanga.*+

Ndimaganiza mumtima mwanga,+

Ndipo ndimafufuza mwakhama.

 7 Kodi Yehova adzatitaya mpaka kalekale?+

Kodi sadzatisonyezanso kukoma mtima kwake?+

 8 Kodi chikondi chake chokhulupirika chatha mpaka kalekale?

Kodi malonjezo ake sadzakwaniritsidwa ku mibadwomibadwo?

 9 Kodi Mulungu waiwala kusonyeza kukoma mtima kwake,+

Kapena kodi mkwiyo wake wachititsa kuti chifundo chake chithe? (Selah)

10 Kodi ndizingonena kuti: “Zimene zikundivutitsa* ndi zakuti:+

Wamʼmwambamwamba wasiya kutithandiza”?

11 Ndidzakumbukira ntchito za Ya,

Ndidzakumbukira zochita zanu zodabwitsa zakale.

12 Ndidzaganizira mozama za ntchito zanu zonse,

Ndipo ndiziganizira mwakuya zochita zanu.+

13 Inu Mulungu, njira zanu ndi zoyera.

Kodi pali mulungu winanso wamkulu amene angafanane ndi inu Mulungu?+

14 Inu ndinu Mulungu woona amene mumachita zinthu zodabwitsa.+

Mwasonyeza ku mitundu ya anthu kuti ndinu wamphamvu.+

15 Ndi mphamvu zanu* mwapulumutsa* anthu anu,+

Ana aamuna a Yakobo ndi a Yosefe. (Selah)

16 Madzi anakuonani, inu Mulungu,

Madzi anakuonani ndipo anavutika.+

Ndipo madzi akuya anayamba kuvutika kwambiri.

17 Mitambo inagwetsa madzi.

Mʼmitambo yakuda munamveka mabingu,

Ndipo mphezi zanu zinawala paliponse ngati mivi.+

18 Phokoso la bingu lanu+ linali ngati la mawilo a galeta.

Kungʼanima kwa mphezi kunaunika padziko lapansi.+

Dziko lapansi linanjenjemera komanso kugwedezeka.+

19 Msewu wanu unadutsa panyanja,+

Ndipo njira yanu inadutsa pamadzi ambiri.

Koma palibe amene anatha kuzindikira mmene mapazi anu anaponda.

20 Munatsogolera anthu anu ngati nkhosa,+

Kudzera mwa Mose ndi Aroni.+

Masikili.* Salimo la Asafu.+

78 Inu anthu anga, mvetserani chilamulo changa.*

Tcherani khutu ku mawu apakamwa panga.

 2 Ndidzatsegula pakamwa panga nʼkunena mwambi.

Ndidzanena mawu ophiphiritsa akalekale.+

 3 Zinthu zimene tinamva ndipo tikuzidziwa,

Zimene makolo athu anatifotokozera,+

 4 Sitidzazibisa kwa ana awo.

Tidzafotokozera mʼbadwo wamʼtsogolo+

Tidzawafotokozera zinthu zotamandika zimene Yehova anachita komanso mphamvu zake,+

Zinthu zodabwitsa zimene wachita.+

 5 Mulungu anaika chikumbutso pakati pa ana a Yakobo,

Ndipo anaika chilamulo mu Isiraeli.

Iye analamula makolo athu

Kuti auze ana awo zinthu zimenezi,+

 6 Kuti mʼbadwo wotsatira,

Ana amene adzabadwe mʼtsogolo, adzadziwe zimenezi.+

Nawonso adzazifotokoze kwa ana awo.+

 7 Zikadzatero anawo azidzadalira Mulungu.

Sadzaiwala ntchito za Mulungu+

Koma azidzasunga malamulo ake.+

 8 Akadzachita zimenezi sadzakhala ngati makolo awo,

Mʼbadwo wosamva komanso wopanduka,+

Mʼbadwo umene mtima wawo unali wosakhazikika*+

Komanso wosakhulupirika kwa Mulungu.

 9 Anthu a fuko la Efuraimu anali ndi mauta,

Koma anathawa pa tsiku lankhondo.

10 Iwo sanasunge pangano la Mulungu,+

Ndipo anakana kutsatira chilamulo chake.+

11 Iwo anaiwalanso zimene anachita,+

Ntchito zake zodabwitsa zimene anawaonetsa.+

12 Mulungu anachita zodabwitsa pamaso pa makolo awo,+

Mʼdziko la Iguputo, mʼdera la Zowani.+

13 Iye anagawa nyanja kuti iwo awoloke,

Ndipo anaimitsa madzi nʼkukhala ngati khoma.+

14 Iye ankawatsogolera ndi mtambo masana

Ndipo usiku wonse ankawatsogolera ndi kuwala kwa moto.+

15 Iye anangʼamba miyala mʼchipululu,

Anawalola kumwa madziwo mpaka ludzu kutha ngati kuti akumwa madzi amʼnyanja.+

16 Iye anatulutsa madzi ochuluka pathanthwe,

Ndipo anachititsa madzi ambiri kuti ayende ngati mitsinje.+

17 Koma iwo anapitiriza kumuchimwira

Popandukira Wamʼmwambamwamba mʼchipululu.+

18 Iwo anayesa Mulungu mʼmitima yawo+

Pomuumiriza kuti awapatse chakudya chimene ankalakalaka.

19 Choncho iwo analankhula mawu amwano kwa Mulungu

Kuti: “Kodi Mulungu angathe kutipatsa chakudya mʼchipululu muno?”+

20 Iye anamenya thanthwe

Moti panatuluka madzi ambiri ndipo mitsinje inasefukira.+

Koma iwo anati: “Kodi angathenso kutipatsa chakudya,

Kapena kodi angapatse anthu ake nyama?”+

21 Yehova atamva zimene ankanenazo anakwiya kwambiri.+

Moto+ unayakira Yakobo,

Ndipo mkwiyo wake unayakira Isiraeli+

22 Chifukwa chakuti sanakhulupirire Mulungu.+

Sanakhulupirire kuti iye angathe kuwapulumutsa.

23 Choncho Mulungu analamula mitambo yamumlengalenga,

Ndipo anatsegula zitseko zakumwamba.

24 Iye anapitiriza kuwagwetsera mana ngati mvula kuti adye.

Anawapatsa tirigu wochokera kumwamba.+

25 Anthu anadya chakudya cha amphamvu.*+

Iye anawapatsa chakudya chokwanira.+

26 Anachititsa kuti mphepo yakumʼmawa iwombe mumlengalenga,

Komanso ndi mphamvu zake, anachititsa kuti mphepo yakumʼmwera iwombe.+

27 Iye anawagwetsera nyama yochuluka ngati fumbi,

Anawagwetsera mbalame zochuluka ngati mchenga wamʼmbali mwa nyanja.

28 Anawagwetsera zimenezi mumsasa wawo,

Kuzungulira matenti awo onse.*

29 Iwo anadya nʼkukhuta kwambiri.

Iye anawapatsa zimene ankalakalaka.+

30 Koma nkhuli yawo isanathe,

Chakudya chawo chidakali mʼkamwa,

31 Mkwiyo wa Mulungu unawayakira.+

Iye anapha amuna amphamvu pakati pawo.+

Anapha anyamata a mu Isiraeli.

32 Ngakhale zinali choncho, iwo anapitiriza kumuchimwira,+

Ndipo sanakhulupirire ntchito zake zodabwitsa.+

33 Choncho anathetsa masiku a moyo wawo ngati mpweya,+

Ndipo anawabweretsera masoka amene anachititsa kuti afe mwadzidzidzi.

34 Nthawi zonse akayamba kuwapha, iwo ankamufunafuna.+

Iwo ankabwerera nʼkuyamba kufunafuna Mulungu,

35 Chifukwa choti ankakumbukira kuti Mulungu anali Thanthwe lawo,+

Ndiponso kuti Mulungu Wamʼmwambamwamba anali Wowawombola.*+

36 Koma iwo ankafuna kumupusitsa ndi pakamwa pawo

Komanso kumunamiza ndi lilime lawo.

37 Mtima wawo sunali wokhulupirika kwa iye.+

Ndipo iwo sanali okhulupirika ku pangano lake.+

38 Koma ankawamvera chifundo.+

Ankawakhululukira* machimo awo ndipo sankawawononga.+

Nthawi zambiri ankabweza mkwiyo wake+

Mʼmalo moonetsa ukali wake wonse.

39 Iye ankakumbukira kuti iwo ndi anthu athupi la nyama,+

Ali ngati mphepo imene imadutsa ndipo sibwereranso.*

40 Nthawi zambiri iwo ankamupandukira mʼchipululu,+

Ndipo ankamukhumudwitsa mʼchipululumo!+

41 Ankayesa Mulungu mobwerezabwereza,+

Ndipo ankachititsa kuti Woyera wa Isiraeli amve chisoni.*

42 Iwo sanakumbukire mphamvu za* Mulungu,

Tsiku limene anawapulumutsa* kwa mdani wawo,+

43 Sanakumbukire mmene anasonyezera zizindikiro zake ku Iguputo,+

Komanso zinthu zodabwitsa zimene anachita mʼdera la Zowani,

44 Sanakumbukirenso mmene anasandutsira madzi amʼngalande zotuluka mumtsinje wa Nailo kukhala magazi,+

Moti sanathe kumwa madziwo.

45 Mulungu anawatumizira ntchentche zoluma kuti ziwasowetse mtendere,+

Komanso achule kuti awawononge.+

46 Anapereka zokolola zawo kwa dzombe lowononga,

Anapereka zipatso za ntchito yawo kwa dzombe lochuluka.+

47 Anawononga mitengo yawo ya mpesa+

Komanso mitengo yawo ya mkuyu ndi matalala.

48 Anapha nyama zawo zonyamula katundu pogwiritsa ntchito matalala,+

Ndiponso ziweto zawo ndi mphezi.

49 Anawasonyeza mkwiyo wake woyaka moto,

Komanso ukali wake ndipo anawabweretsera mavuto,

Anawatumizira magulu a angelo kuti awabweretsere tsoka.

50 Mkwiyo wake anaulambulira njira.

Sanawapulumutse ku imfa,

Ndipo anawagwetsera mliri.*

51 Pamapeto pake anapha ana onse oyamba kubadwa a ku Iguputo,+

Amene ndi chiyambi cha mphamvu zawo zobereka mʼmatenti a Hamu.

52 Kenako anatulutsa anthu ake mʼdzikolo ngati gulu la nkhosa,+

Ndipo anawatsogolera mʼchipululu ngati nkhosa.

53 Anawatsogolera ndi kuwateteza,

Ndipo sanachite mantha.+

Nyanja inamiza adani awo.+

54 Kenako anawalowetsa mʼdziko lake lopatulika,+

Mʼdera lamapiri ili limene dzanja lake lamanja linatenga.+

55 Iye anathamangitsa mitundu ya anthu kuichotsa pamaso pawo.+

Iye anawagawira dzikolo kuti likhale cholowa chawo pochita kuwayezera ndi chingwe.+

Anachititsa mafuko a Isiraeli kuti akhale mʼnyumba zawozawo.+

56 Koma iwo anapitiriza kuyesa Mulungu Wamʼmwambamwamba komanso kumupandukira.+

Sanamvere zikumbutso zake.+

57 Iwo anasiyanso Mulungu ndipo ankachita zinthu mwachinyengo ngati makolo awo.+

Anali osadalirika ngati uta wosakunga kwambiri.+

58 Anapitiriza kumukhumudwitsa ndi malo awo okwezeka,+

Ndipo anamukwiyitsa* ndi zifaniziro zawo zogoba.+

59 Mulungu anamva ndipo anakwiya kwambiri,+

Choncho anawakaniratu Aisiraeli.

60 Pamapeto pake anasiya chihema cha ku Silo,+

Tenti imene ankakhalamo pakati pa anthu.+

61 Analola kuti adani atenge chizindikiro cha mphamvu zake,

Analola kuti ulemerero wake ukhale mʼmanja mwa adani.+

62 Iye anapereka anthu ake ku lupanga,+

Ndipo anakwiyira cholowa chake.

63 Moto unapsereza anyamata ake,

Ndipo anamwali ake sanawaimbire nyimbo zapaukwati.*

64 Ansembe ake anaphedwa ndi lupanga,+

Ndipo akazi awo amasiye sanalire.+

65 Kenako Yehova anadzuka ngati kuti anali mtulo,+

Ngati mmene amadzukira munthu wamphamvu+ pambuyo pomwa vinyo wambiri.

66 Iye anathamangitsa adani ake nʼkuwabweza,+

Anachititsa kuti adaniwo akhale onyozeka mpaka kalekale.

67 Iye anakana tenti ya Yosefe,

Ndipo sanasankhe fuko la Efuraimu.

68 Koma anasankha fuko la Yuda,+

Phiri la Ziyoni limene amalikonda.+

69 Anachititsa kuti malo ake opatulika akhalepo mpaka kalekale ngati kumwamba,*+

Ngati dziko lapansi limene analikhazikitsa mpaka kalekale.+

70 Anasankha Davide+ mtumiki wake,

Ndipo anamuchotsa kumakola a nkhosa,+

71 Kumene ankaweta nkhosa zoyamwitsa,

Anamuika kuti akhale mʼbusa wa ana a Yakobo, omwe ndi anthu ake,+

Ndi Isiraeli, amene ndi cholowa chake.+

72 Iye anawaweta ndi mtima wokhulupirika,+

Ndipo anawatsogolera mwaluso.+

Nyimbo ya Asafu.+

79 Inu Mulungu, anthu a mitundu ina alowa mʼdziko limene ndi cholowa chanu.+

Aipitsa kachisi wanu woyera.+

Yerusalemu amusandutsa bwinja.+

 2 Apereka mitembo ya atumiki anu kwa mbalame kuti chikhale chakudya chawo

Ndipo matupi a anthu anu okhulupirika awapereka kwa zilombo zakutchire.+

 3 Atsanula magazi awo ngati madzi kuzungulira Yerusalemu,

Ndipo palibe aliyense amene watsala kuti awaike mʼmanda.+

 4 Anthu oyandikana nafe akutinyoza,+

Anthu otizungulira akutiseka komanso kutikuwiza.

 5 Inu Yehova, kodi mukhala wokwiya mpaka liti? Kwamuyaya?+

Kodi mkwiyo wanu ukhala ukuyaka ngati moto mpaka liti?+

 6 Tsanulirani mkwiyo wanu pa mitundu ya anthu amene sakukudziwani

Komanso pa maufumu amene saitana pa dzina lanu.+

 7 Chifukwa iwo awononga mbadwa zonse za Yakobo

Ndipo dziko lawo alisandutsa bwinja.+

 8 Musatiimbe mlandu chifukwa cha zolakwa za makolo athu.+

Tisonyezeni chifundo chanu mofulumira,+

Chifukwa zativuta kwambiri.

 9 Tithandizeni inu Mulungu amene mumatipulumutsa,+

Chifukwa cha dzina lanu laulemerero.

Tipulumutseni komanso mutikhululukire* machimo athu chifukwa cha dzina lanu.+

10 Musalole kuti anthu a mitundu ina azinena kuti: “Mulungu wawo ali kuti?”+

Anthu a mitundu ina adziwe ife tikuona

Kuti mwabwezera magazi a atumiki anu amene anakhetsedwa.+

11 Imvani kuusa moyo kwa mkaidi.+

Gwiritsani ntchito mphamvu zanu zazikulu* kupulumutsa anthu amene aweruzidwa kuti aphedwe.*+

12 Bwezerani anthu oyandikana nafe maulendo 7+

Chifukwa choti akunyozani, inu Yehova.+

13 Mukatero, ife anthu anu komanso nkhosa zimene mukuweta,+

Tidzakuyamikani mpaka kalekale.

Ndipo tidzalengeza kuti inu ndi woyenera kutamandidwa ku mibadwomibadwo.+

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimboyi iimbidwe motsatira kaimbidwe ka “Nyimbo ya Maluwa.” Chikumbutso. Nyimbo ndi Salimo la Asafu.+

80 Inu Mʼbusa wa Isiraeli, mvetserani,

Inu amene mukutsogolera Yosefe ngati gulu la nkhosa.+

Inu amene mwakhala pampando wachifumu pamwamba* pa akerubi,+

Onetsani kuwala kwanu.*

 2 Sonyezani mphamvu zanu+

Pa Efuraimu, Benjamini ndi Manase.

Bwerani mudzatipulumutse.+

 3 Inu Mulungu, tibwezeretseni mwakale.+

Walitsani nkhope yanu pa ife kuti tipulumutsidwe.+

 4 Inu Yehova Mulungu wa magulu ankhondo akumwamba, kodi mudzakwiyira* anthu anu nʼkukana kumvetsera mapemphero awo mpaka liti?+

 5 Mwawapatsa misozi kuti ikhale chakudya chawo,

Ndipo mukuwamwetsa misozi yochuluka kwambiri.

 6 Mwachititsa kuti anthu oyandikana nafe azikanganirana ifeyo.

Adani athu akupitirizabe kutinyoza mmene akufunira.+

 7 Inu Mulungu wa magulu ankhondo akumwamba, tibwezeretseni mwakale.

Walitsani nkhope yanu pa ife kuti tipulumutsidwe.+

 8 Munachititsa kuti mtengo wa mpesa+ uchoke mu Iguputo.

Munathamangitsa mitundu ya anthu kuti mudzalemo mtengowo.+

 9 Munalambula malo odzalapo mtengo wa mpesawo,

Ndipo unazika mizu nʼkudzaza dziko.+

10 Mapiri anaphimbika ndi mthunzi wake,

Ndipo mitengo yamkungudza ya Mulungu inaphimbika ndi nthambi zake.

11 Nthambi zake zinakafika mpaka kunyanja,

Ndipo mphukira zake zinafika ku Mtsinje.*+

12 Nʼchifukwa chiyani mwagwetsa mpanda wamiyala wa munda wampesawo,+

Kuti anthu onse odutsa mumsewu azithyola zipatso zake?+

13 Nguluwe zamʼnkhalango zikuwononga mtengowo,

Ndipo nyama zakutchire zikuudya.+

14 Inu Mulungu wa magulu ankhondo akumwamba, chonde bwererani.

Yangʼanani pansi pano muli kumwambako kuti muone,

Ndipo samalirani mtengo wa mpesa uwu,+

15 Mtengo umene dzanja lanu lamanja ladzala.+

Ndipo muone mwana wanu amene munamupatsa* mphamvu kuti inu mulemekezeke.+

16 Wawotchedwa ndi moto+ nʼkudulidwa.

Anthu amawonongeka ndi kudzudzula kwanu.*

17 Dzanja lanu lithandize munthu amene ali kudzanja lanu lamanja,

Lithandize mwana wa munthu amene mwamupatsa mphamvu kuti mulemekezeke.+

18 Mukatero ife sitidzakusiyani.

Tithandizeni kuti tikhalebe ndi moyo kuti titamande dzina lanu.

19 Inu Yehova Mulungu wa magulu ankhondo akumwamba, tibwezeretseni mwakale.

Walitsani nkhope yanu pa ife kuti tipulumutsidwe.+

Kwa wotsogolera nyimbo, pa Gititi.* Salimo la Asafu.+

81 Fuulani mosangalala kwa Mulungu amene ndi mphamvu yathu.+

Fuulirani Mulungu wa Yakobo mosangalala chifukwa wapambana.

 2 Yambani kuimba nyimbo ndipo tengani maseche,

Zeze womveka mosangalatsa pamodzi ndi choimbira cha zingwe.

 3 Pa tsiku limene mwezi watsopano waoneka,+ imbani lipenga la nyanga ya nkhosa,

Pa tsiku limene mwezi wathunthu waoneka, imbani lipenga la nyanga ya nkhosa, limene limaimbidwa pa tsiku la chikondwerero.+

 4 Chifukwa limeneli ndi lamulo kwa Isiraeli,

Komanso chigamulo cha Mulungu wa Yakobo.+

 5 Mulungu anaika chigamulocho kuti chikhale chikumbutso kwa Yosefe+

Pamene ankapita kukapereka chilango mʼdziko la Iguputo.+

Ndinamva mawu amene sindinathe kuwazindikira akuti:*

 6 “Ndinachotsa katundu wolemera paphewa lake.+

Manja ake anamasuka moti sankanyamulanso dengu.

 7 Pamene unkakumana ndi mavuto unaitana, ndipo ine ndinakupulumutsa.+

Ndinakuyankha ndi mabingu ochokera mumtambo.*+

Ndinakuyesa pamadzi a ku Meriba.*+ (Selah)

 8 Imvani anthu anga, ndipo ine ndipereka umboni wokutsutsani.

Inu Aisiraeli, zikanakhala bwino ngati mukanandimvera.+

 9 Pakati panu sipadzakhala mulungu wachilendo,

Ndipo simudzagwadira mulungu wachilendo.+

10 Ine Yehova, ndine Mulungu wanu,

Amene ndinakutulutsani mʼdziko la Iguputo.+

Tsegulani kwambiri pakamwa panu ndipo ndidzaikamo chakudya.+

11 Koma anthu anga sanamvere mawu anga,

Isiraeli sanafune kundigonjera.+

12 Choncho ndinawasiya kuti apitirize kuchita zofuna za mtima wawo wosamverawo.

Iwo anachita zimene ankaganiza kuti nʼzoyenera.*+

13 Zikanakhala bwino ngati anthu anga akanandimvera,+

Zikanakhala bwino ngati Isiraeli akanayenda mʼnjira zanga.+

14 Ndikanagonjetsa adani awo mofulumira,

Ndikanalanga adani awo ndi dzanja langa.+

15 Amene amadana ndi Yehova adzachita mantha pamaso pake,

Ndipo zimene zidzawachitikire* zidzakhalapo mpaka kalekale.

16 Koma iye adzakudyetsani tirigu wabwino kwambiri,*+

Ndipo adzakupatsani uchi wochokera pathanthwe kuti mudye nʼkukhuta.”+

Nyimbo ya Asafu.+

82 Mulungu waima pamsonkhano wake,*+

Akuweruza pakati pa milungu* kuti:+

 2 “Kodi mupitiriza kuweruza mopanda chilungamo+

Komanso kukondera anthu oipa mpaka liti?+ (Selah)

 3 Tetezani* anthu onyozeka ndi ana amasiye.+

Chitirani chilungamo anthu amene alibe wowathandiza komanso osauka.+

 4 Pulumutsani munthu wonyozeka ndi wosauka.

Alanditseni mʼmanja mwa anthu oipa.”

 5 Milunguyo sikudziwa kapena kuzindikira.+

Ikuyendayenda mumdima,

Maziko onse a dziko lapansi agwedezeka.+

 6 “Ine ndanena kuti, ‘Inu ndinu milungu,*+

Nonsenu ndinu ana a Wamʼmwambamwamba.

 7 Koma mudzafa ngati mmene anthu onse amafera.+

Ndipo mudzagwa ngati mmene kalonga aliyense amagwera!’”+

 8 Nyamukani inu Mulungu, ndipo muweruze dziko lapansi,+

Chifukwa mitundu yonse ya anthu ndi yanu.

Nyimbo ndi Salimo la Asafu.+

83 Inu Mulungu, musakhale chete.+

Musakhale chete osalankhula kanthu kapena kuchita chilichonse, inu Mulungu.

 2 Taonani! Adani anu akuchita phokoso.+

Anthu amene amadana nanu akuchita zinthu modzikuza.*

 3 Mwachinsinsi komanso mochenjera iwo amakonzera chiwembu anthu anu.

Iwo amakonzera chiwembu anthu anu omwe ndi amtengo wapatali.*

 4 Iwo akunena kuti: “Bwerani tiwawononge kuti asakhalenso mtundu,+

Kuti dzina la Isiraeli lisadzakumbukiridwenso.”

 5 Mogwirizana iwo amapangana zoti achite,*

Iwo apanga mgwirizano* kuti atsutsane ndi inu+—

 6 Aedomu, mbadwa za Isimaeli, Amowabu+ komanso mbadwa za Hagara,+

 7 Agebala, Aamoni,+ Aamaleki,

Afilisiti+ pamodzi ndi anthu a ku Turo.+

 8 Asuri nawonso agwirizana nawo,+

Ndipo amathandiza* ana aamuna a Loti.+ (Selah)

 9 Muwachitire zimene munachitira Midiyani,+

Komanso zimene munachitira Sisera ndi Yabini kumtsinje wa Kisoni.*+

10 Iwo anawonongedwa ku Eni-dori.+

Anasanduka manyowa munthaka.

11 Anthu awo olemekezeka muwachititse kukhala ngati Orebi ndi Zeebi.+

Ndipo akalonga* awo muwachititse kukhala ngati Zeba ndi Zalimuna.+

12 Chifukwa iwo anena kuti: “Tiyeni tilande dziko limene Mulungu amakhala.”

13 Inu Mulungu wanga, achititseni kukhala ngati udzu wouma wouluzika ndi mphepo,+

Ngati mapesi amene amauluka ndi mphepo.

14 Ngati moto umene umayatsa nkhalango,

Ngati malawi a moto umene ukuyaka mʼmapiri,+

15 Muwathamangitse ndi mphepo yanu yamphamvu,+

Ndipo muwaopseze ndi mphepo yanu yamkuntho.+

16 Phimbani* nkhope zawo ndi manyazi,

Kuti afunefune dzina lanu, inu Yehova.

17 Achititsidwe manyazi ndipo akhale ndi mantha mpaka kalekale.

Anyozeke ndipo atheretu.

18 Anthu adziwe kuti inu, amene dzina lanu ndinu Yehova,+

Inu nokha ndinu Wamʼmwambamwamba, woyenera kulamulira dziko lonse lapansi.+

Kwa wotsogolera nyimbo, pa Gititi.* Nyimbo ndi Salimo la ana a Kora.+

84 Inu Yehova wa magulu ankhondo akumwamba,

Ine ndimakonda kwambiri chihema chanu chachikulu!+

 2 Moyo wanga ukulakalaka kwambiri,

Inde, ndafookeratu chifukwa cholakalaka

Mabwalo a Yehova.+

Mtima wanga ndi thupi langa zikufuula mosangalala kwa Mulungu wamoyo.

 3 Ngakhale mbalame zapeza malo okhala kumeneko

Ndipo namzeze wadzimangira chisa chake,

Mmene amasamaliramo ana ake

Pafupi ndi guwa lanu lansembe lalikulu, inu Yehova wa magulu ankhondo akumwamba,

Mfumu yanga ndi Mulungu wanga!

 4 Osangalala ndi anthu amene akukhala mʼnyumba yanu!+

Iwo akupitiriza kukutamandani.+ (Selah)

 5 Osangalala ndi anthu amene amapeza mphamvu kuchokera kwa inu,+

Amene mitima yawo imalakalaka misewu yaikulu yopita kunyumba yanu.

 6 Akamadutsa mʼchigwa cha Baka,*

Amasandutsa chigwacho kukhala malo opezeka akasupe.

Ndipo mvula yoyambirira imabweretsa madalitso mʼchigwacho.

 7 Mphamvu zawo zidzapitiriza kuwonjezeka pamene akuyenda.+

Aliyense wa iwo amaonekera pamaso pa Mulungu mu Ziyoni.

 8 Inu Yehova Mulungu wa magulu ankhondo akumwamba, imvani pemphero langa.

Mvetserani, inu Mulungu wa Yakobo. (Selah)

 9 Inu Mulungu wathu komanso chishango chathu,+ onani,*

Yangʼanani nkhope ya wodzozedwa wanu.+

10 Kukhala tsiku limodzi mʼmabwalo anu nʼkwabwino kuposa kukhala kwinakwake masiku 1,000!+

Ndasankha kuima pakhomo la nyumba ya Mulungu wanga

Kuposa kukhala mʼmatenti a anthu oipa.

11 Chifukwa Yehova Mulungu ndi dzuwa+ ndiponso chishango.+

Iye amatikomera mtima nʼkutipatsa ulemerero.

Yehova sadzalephera kupereka chinthu chilichonse chabwino

Kwa anthu amene amachita zinthu mokhulupirika.+

12 Inu Yehova wa magulu ankhondo akumwamba,

Wosangalala ndi munthu amene amakukhulupirirani.+

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ndi Salimo la ana a Kora.+

85 Inu Yehova, dziko lanu mwalisonyeza kukoma mtima.+

Mwabwezeretsa ana a Yakobo amene anagwidwa ukapolo.+

 2 Munakhululukira anthu anu zolakwa zawo.

Munawakhululukira* machimo awo onse.+ (Selah)

 3 Munabweza mkwiyo wanu wonse,

Ndipo simunasonyeze mkwiyo wanu waukulu.+

 4 Tibwezeretseni mwakale,* inu Mulungu amene mumatipulumutsa,

Ndipo tichotsereni mkwiyo wanu.+

 5 Kodi mutikwiyira mpaka kalekale?+

Kodi mudzapitiriza kusonyeza mkwiyo wanu ku mibadwomibadwo?

 6 Kodi simutipatsanso mphamvu

Kuti anthu anu asangalale chifukwa cha inu?+

 7 Tisonyezeni chikondi chanu chokhulupirika inu Yehova,+

Ndipo mutipulumutse.

 8 Ndidzamvetsera zimene Mulungu woona Yehova adzanene,

Chifukwa adzanena za mtendere kwa anthu ake,+ kwa okhulupirika ake.

Koma iwo asayambenso kudzidalira kwambiri ngati kale.+

 9 Ndithudi, iye ndi wokonzeka kupulumutsa amene amamuopa,+

Kuti ulemerero wake ukhale mʼdziko lathu.

10 Chikondi chokhulupirika komanso kukhulupirika zidzakumana.

Chilungamo ndi mtendere zidzakisana.+

11 Kukhulupirika kudzaphuka padziko lapansi,

Ndipo chilungamo chidzayangʼana pansi kuchokera kumwamba.+

12 Ndithudi, Yehova adzapereka zinthu zabwino,*+

Ndipo dziko lathu lidzapereka zokolola zake.+

13 Chilungamo chidzayenda pamaso pake,+

Ndipo chidzapanga njira kuti mapazi a Mulungu azidutsamo.

Pemphero la Davide.

86 Tcherani khutu* inu Yehova ndipo mundiyankhe,

Chifukwa ndavutika komanso ndasauka.+

 2 Tetezani moyo wanga chifukwa ndine wokhulupirika.+

Pulumutsani mtumiki wanu amene amakukhulupirirani,

Chifukwa ndinu Mulungu wanga.+

 3 Ndikomereni mtima inu Yehova,+

Chifukwa ndimaitana inu tsiku lonse.+

 4 Chititsani kuti mtumiki wanu asangalale,*

Chifukwa ndimayangʼana kwa inu, Yehova.

 5 Inu Yehova ndinu wabwino+ ndipo ndinu wokonzeka kukhululuka.+

Mumasonyeza chikondi chokhulupirika chochuluka kwa onse amene amaitana inu.+

 6 Mvetserani pemphero langa inu Yehova.

Ndipo mvetserani kuchonderera kwanga kopempha thandizo.+

 7 Pa tsiku limene ndakumana ndi mavuto ndidzaitana inu,+

Chifukwa inu mudzandiyankha.+

 8 Inu Yehova, palibe mulungu wina amene angafanane ndi inu,+

Palibe aliyense amene wachita zinthu zofanana ndi zimene inu mwachita.+

 9 Mitundu yonse ya anthu imene munapanga

Idzabwera nʼkudzagwada pamaso panu, inu Yehova,+

Ndipo idzalemekeza dzina lanu.+

10 Chifukwa inu ndinu wamkulu ndipo mumachita zinthu zodabwitsa.+

Inu nokha ndinu Mulungu.+

11 Ndilangizeni inu Yehova, za njira yanu.+

Kuti ndiyende mʼchoonadi chanu.+

Ndithandizeni kuti ndiziopa dzina lanu ndi mtima wonse.*+

12 Ndimakutamandani ndi mtima wanga wonse, inu Yehova Mulungu wanga,+

Ndipo ndidzalemekeza dzina lanu mpaka kalekale,

13 Chifukwa chikondi chanu chokhulupirika chimene mumandisonyeza ndi chachikulu

Ndipo mwapulumutsa moyo wanga ku dzenje la Manda.*+

14 Inu Mulungu, anthu onyada andiukira.+

Gulu la anthu ankhanza likufuna kuchotsa moyo wanga,

Ndipo iwo sakulemekezani.*+

15 Koma inu Yehova, ndinu Mulungu wachifundo komanso wokoma mtima,

Wosakwiya msanga, wachikondi chokhulupirika chochuluka ndiponso wokhulupirika.*+

16 Ndiyangʼaneni ndipo mundikomere mtima.+

Patsani mtumiki wanu mphamvu,+

Ndipo pulumutsani mwana wa kapolo wanu wamkazi.

17 Ndisonyezeni chizindikiro cha* ubwino wanu,

Kuti anthu amene amadana nane aone ndipo achititsidwe manyazi,

Chifukwa inu Yehova ndi amene mumandithandiza komanso kundilimbikitsa.

Nyimbo ndi Salimo la ana a Kora.+

87 Maziko a mzinda wa Mulungu ali mʼmapiri opatulika.+

 2 Yehova amakonda kwambiri mageti a Ziyoni+

Kuposa matenti onse a Yakobo.

 3 Iwe mzinda wa Mulungu woona, anthu akunena za ulemerero wako.+ (Selah)

 4 Ndidzaika Rahabi* ndi Babulo mʼgulu la amene+ akundidziwa.

Filisitiya, Turo ndi Kusi alinso mʼgulu la amene akundidziwa.

Ine ndidzati: “Amenewa anabadwira mʼZiyoni.”

 5 Ponena za Ziyoni anthu adzati:

“Aliyense anabadwira mmenemo.”

Ndipo Wamʼmwambamwamba adzakhazikitsa mzinda umenewo ndi kuulimbitsa.

 6 Powerenga mitundu ya anthu, Yehova adzalengeza kuti:

“Amenewa anabadwira mu Ziyoni.” (Selah)

 7 Oimba+ komanso ovina magule amene amavina mozungulira+ adzanena kuti:

“Akasupe anga onse ali mwa iwe.”*+

Nyimbo ndi Salimo la ana a Kora.+ Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimboyi iimbidwe potsatira kaimbidwe ka Mahalati* ndipo iimbidwe molandizana. Masikili* ya Hemani+ wa mʼbanja la Zera.

88 Inu Yehova, Mulungu amene amandipulumutsa,+

Masana ndimafuulira inu,

Ndipo usiku ndimabwera pamaso panu.+

 2 Pemphero langa lifike kwa inu.+

Tcherani khutu lanu kuti mumve* kuchonderera kwanga kopempha thandizo.+

 3 Chifukwa moyo wanga wadzaza ndi masoka,+

Ndipo moyo wanga wayandikira ku Manda.*+

 4 Anandiika kale mʼgulu la anthu amene akutsikira kudzenje.*+

Ndakhala munthu wovutika,*+

 5 Amene wasiyidwa pakati pa anthu akufa

Ngati anthu ophedwa amene agona mʼmanda,

Amene simukuwakumbukiranso

Komanso amene sakuthandizidwa ndi inu.*

 6 Mwandiika mʼdzenje lakuya kwambiri,

Mʼmalo amdima, mʼphompho lalikulu.

 7 Mkwiyo wanu ukundilemera kwambiri,+

Ndipo ndikumva ngati mukundipanikiza ndi mafunde anu amphamvu. (Selah)

 8 Anzanga mwawathamangitsira kutali ndi ine.+

Mwandipangitsa kuti ndikhale chinthu chonyansa kwa iwo.

Ndakodwa ndipo sindingathe kuthawa.

 9 Diso langa lachita mdima chifukwa cha kuvutika kwanga.+

Ndimaitana inu Yehova tsiku lonse.+

Ndimapemphera kwa inu nditakweza manja anga.

10 Kodi mungachitire zinthu zodabwitsa anthu akufa?

Kodi anthu akufa amene sangathe kuchita kanthu angadzuke nʼkukutamandani?+ (Selah)

11 Kodi chikondi chanu chokhulupirika chingalengezedwe kumanda?

Kodi kukhulupirika kwanu kungalengezedwe mʼmalo a chiwonongeko?*

12 Kodi ntchito zanu zodabwitsa zingadziwike mu mdima?

Kapena kodi chilungamo chanu chidzadziwika mʼdziko la anthu oiwalika?+

13 Koma ine ndimafuulirabe kwa inu Yehova kuti mundithandize,+

Mʼmawa uliwonse pemphero langa limafika kwa inu.+

14 Inu Yehova, nʼchifukwa chiyani mukundikana?+

Nʼchifukwa chiyani mukundibisira nkhope yanu?+

15 Kuyambira ndili mnyamata,

Ndakhala ndikuzunzika komanso kutsala pangʼono kufa.+

Ndafooka kwambiri chifukwa cha zinthu zoopsa zimene mwalola kuti ndikumane nazo.

16 Ndafooka chifukwa cha mkwiyo wanu woyaka moto.+

Zinthu zochititsa mantha zochokera kwa inu zandiwononga.

17 Zinthu zimene mumachita zandizungulira ngati madzi tsiku lonse.

Zanditsekera kuzungulira mbali zonse.

18 Anzanga komanso anthu oyandikana nawo mwawathamangitsira kutali ndi ine.+

Malo amdima akhala mnzanga wapamtima.

Masikili.* Salimo la Etani+ wa mʼbanja la Zera.

89 Ndidzaimba mpaka kalekale za mmene Yehova wasonyezera chikondi chake chokhulupirika.

Ndidzalengeza ndi pakamwa panga za kukhulupirika kwanu ku mibadwo yonse.

 2 Chifukwa ndanena kuti: “Chikondi chanu chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale,+

Ndipo kukhulupirika kwanu kudzakhala kumwamba mpaka kalekale.”

 3 Mulungu anati: “Ndachita pangano ndi wosankhidwa wanga.+

Ndalumbira kwa Davide mtumiki wanga kuti:+

 4 ‘Ndidzachititsa kuti mbadwa* zako zikhalepo mpaka kalekale,+

Ndipo ndidzachititsa kuti ufumu* wako ukhalepo ku mibadwo yonse.’”+ (Selah)

 5 Inu Yehova, kumwamba kudzakutamandani chifukwa cha ntchito zanu zodabwitsa,

Mpingo wa oyera anu udzakutamandani chifukwa ndinu wokhulupirika.

 6 Ndi ndani kumwamba amene angafanane ndi Yehova?+

Ndi ndani pakati pa ana a Mulungu+ amene ndi wofanana ndi Yehova?

 7 Mulungu ndi wochititsa mantha komanso wolemekezeka pakati pa gulu lake la oyera.*+

Iye ndi wamkulu komanso wochititsa mantha kwa onse amene amuzungulira.+

 8 Inu Yehova Mulungu wa magulu ankhondo akumwamba,

Ndi ndani ali ndi mphamvu ngati inu Ya?+

Ndinu wokhulupirika pa chilichonse.+

 9 Nyanja ikadzaza mumailamulira.+

Mafunde ake akawinduka, inuyo mumawachititsa kuti akhale bata.+

10 Mwaphwanya Rahabi*+ ngati munthu amene waphedwa.+

Mwabalalitsa adani anu ndi dzanja lanu lamphamvu.+

11 Kumwamba ndi kwanu, dziko lapansi ndi lanunso.+

Nthaka ya dziko lapansi ndiponso zinthu zimene zili mmenemo+ munazipanga ndinu.

12 Munapanga kumpoto ndi kumʼmwera.

Mapiri a Tabori+ ndi Herimoni+ amatamanda dzina lanu mosangalala.

13 Mkono wanu ndi wamphamvu,+

Dzanja lanu ndi lamphamvu,+

Dzanja lanu lamanja lapambana.+

14 Mukamalamulira, nthawi zonse mumachita zinthu mwachilungamo komanso molungama.+

Nthawi zonse mumasonyeza kukhulupirika komanso chikondi chokhulupirika.+

15 Osangalala ndi anthu amene amakutamandani ndi mawu osangalala.+

Iwo amayenda mʼkuwala kwa nkhope yanu, inu Yehova.

16 Chifukwa cha dzina lanu, iwo amasangalala tsiku lonse,

Ndipo amalemekezedwa chifukwa cha chilungamo chanu.

17 Mumachititsa kuti anthu anu akhale amphamvu komanso kuti alemekezedwe,+

Ndipo mphamvu* zathu zikuwonjezeka, chifukwa chakuti mukusangalala nafe.+

18 Chifukwa chishango chathu ndi chochokera kwa Yehova,

Ndipo mfumu yathu ndi yochokera kwa Woyera wa Isiraeli.+

19 Pa nthawi imeneyo munalankhula mʼmasomphenya kwa okhulupirika anu ndipo munati:

“Ndapereka nyonga kwa wamphamvu.+

Ndakweza wosankhidwa mwapadera pakati pa anthu.+

20 Ndapeza Davide mtumiki wanga,+

Ndipo ndamudzoza ndi mafuta anga opatulika.+

21 Dzanja langa lidzamuthandiza,+

Ndipo mkono wanga udzamulimbitsa.

22 Palibe mdani amene adzamukakamize kuti apereke msonkho,

Ndipo palibe munthu woipa amene adzamupondereze.+

23 Ndidzaphwanya adani ake kuti akhale zidutswazidutswa iye akuona.+

Ndipo ndidzapha amene amadana naye.+

24 Kukhulupirika kwanga komanso chikondi changa chokhulupirika zili pa iye,+

Ndipo ndidzachititsa kuti akhale ndi mphamvu* chifukwa cha dzina langa.

25 Ndidzaika ulamuliro wake* panyanja

Ndipo ndidzamʼpatsa ulamuliro pamitsinje.+

26 Iye adzafuula kwa ine kuti: ‘Inu ndinu Bambo anga,

Mulungu wanga komanso Thanthwe la chipulumutso changa.’+

27 Ndipo ndidzamuika kuti akhale ngati mwana woyamba kubadwa,+

Ndiponso mfumu yaikulu pa mafumu onse apadziko lapansi.+

28 Ndidzapitiriza kumusonyeza chikondi changa chokhulupirika mpaka kalekale,+

Ndipo pangano limene ndinachita naye silidzaphwanyidwa.+

29 Ndidzachititsa kuti mbadwa* zake zidzakhalepo kwamuyaya,

Ndipo ndidzachititsa kuti mpando wake wachifumu udzakhalepo mpaka kalekale ngati kumwamba.+

30 Ana ake akadzasiya chilamulo changa,

Ndipo akadzaleka kutsatira zigamulo* zanga,

31 Akadzaphwanya mfundo zanga

Komanso osasunga malamulo anga,

32 Ine ndidzawalanga ndi ndodo chifukwa cha kusamvera* kwawo,+

Ndipo ndidzawakwapula chifukwa cha zolakwa zawo.

33 Koma sindidzasiya kumusonyeza chikondi changa chokhulupirika,+

Kapena kulephera kukwaniritsa lonjezo langa.*

34 Sindidzaphwanya pangano langa+

Kapena kusintha mawu otuluka pakamwa panga.+

35 Ndalumbira kamodzi kokha pa kuyera kwanga.

Davide sindidzamunamiza.+

36 Mbadwa* zake zidzakhalapo mpaka kalekale,+

Ndipo mpando wake wachifumu udzakhala pamaso panga kwamuyaya ngati dzuwa.+

37 Udzakhalapo mpaka kalekale ngati mwezi

Udzakhala ngati mboni yokhulupirika yamumlengalenga.” (Selah)

38 Koma inu mwataya wodzozedwa wanu ndipo mwamukana,+

Komanso mwamukwiyira kwambiri.

39 Mwakana monyansidwa pangano la mtumiki wanu.

Mwanyoza chisoti chake chachifumu pochiponyera pansi.

40 Mwagwetsa mipanda yake yonse yamiyala.*

Mizinda yake ya mipanda yolimba mwaisandutsa mabwinja.

41 Anthu onse amene amadutsa njira imeneyo alanda zinthu zake.

Iye akunyozedwa ndi anthu oyandikana naye.+

42 Mwachititsa kuti adani ake apambane.*+

Mwachititsa kuti adani ake onse asangalale.

43 Mwachititsanso kuti lupanga lake likhale lopanda ntchito,

Ndipo mwachititsa kuti iye asapambane pa nkhondo.

44 Mwathetsa ulemerero wake,

Ndipo mpando wake wachifumu mwauponyera pansi.

45 Mwafupikitsa masiku a unyamata wake.

Ndipo mwamuveka manyazi. (Selah)

46 Inu Yehova, kodi mudzadzibisa mpaka liti? Mpaka kalekale?+

Kodi mkwiyo wanu udzapitiriza kuyaka ngati moto?

47 Kumbukirani kuti moyo wanga ndi waufupi.+

Kodi anthu munawalenga popanda cholinga?

48 Kodi pali munthu aliyense amene angapitirize kukhala ndi moyo ndipo sadzafa?+

Kodi angathe kupulumutsa moyo wake ku mphamvu ya Manda?* (Selah)

49 Inu Yehova, kodi zochita zanu zakale zosonyeza chikondi chanu chokhulupirika zili kuti,

Zimene munalumbira kwa Davide chifukwa cha kukhulupirika kwanu?+

50 Inu Yehova, kumbukirani mmene atumiki anu anyozedwera.

Kumbukirani mmene ndapiririra* kunyozedwa kochokera ku mitundu yonse ya anthu.

51 Inu Yehova, kumbukirani mmene adani anu alankhulira monyoza.

Mmene anyozera paliponse pamene mapazi a wodzozedwa wanu aponda.

52 Yehova atamandike mpaka kalekale. Ame! Ame!+

BUKU LA 4

(Masalimo 90-106)

Pemphero la Mose, munthu wa Mulungu woona.+

90 Inu Yehova, mwakhala malo athu okhalamo+ ku mibadwo yonse.

 2 Mapiri asanabadwe,

Kapena musanakhazikitse dziko lapansi komanso nthaka,+

Inu ndinu Mulungu kuyambira kalekale mpaka kalekale.+

 3 Mumabwezera munthu kufumbi,

Mumanena kuti: “Bwererani kufumbi, inu ana a anthu.”+

 4 Chifukwa kwa inu zaka 1,000 zili ngati dzulo lapitali,+

Zili ngati ulonda umodzi wa usiku.

 5 Mumawawononga+ ndipo amatha ngati tulo.

Mʼmawa amakhala ngati msipu umene waphukira.+

 6 Mʼmawa umaphuka ndipo umabiriwira,

Koma madzulo umafota kenako nʼkuuma.+

 7 Chifukwa ife tawonongedwa ndi mkwiyo wanu,+

Ndipo tikuchita mantha kwambiri ndi ukali wanu.

 8 Mumaika zolakwa zathu patsogolo panu,*+

Zinsinsi zathu zaululika chifukwa cha kuwala kwa nkhope yanu.+

 9 Moyo wathu ukutha chifukwa cha mkwiyo wanu.

Timafa msanga ngati mpweya umene umatha mofulumira.

10 Masiku a moyo wathu amangokwana zaka 70

Kapena 80+ ngati munthu ali ndi mphamvu zambiri.*

Koma zimakhala zodzaza ndi mavuto komanso chisoni.

Zimatha mofulumira ndipo moyo wathu umachoka.+

11 Ndi ndani angadziwe kuchuluka kwa mphamvu za mkwiyo wanu?

Ukali wanu ndi waukulu mofanana ndi mantha amene tikuyenera kukusonyezani.+

12 Tiphunzitseni mmene tingagwiritsire ntchito bwino moyo wathu*+

Kuti tikhale ndi mtima wanzeru.

13 Bwererani, inu Yehova!+ Kodi zinthu zikhala chonchi mpaka liti?+

Timvereni chisoni ife atumiki anu.+

14 Mʼmawa, muzitisonyeza chikondi chanu chokhulupirika,+

Kuti tizifuula mokondwera komanso kukhala mosangalala+ masiku onse a moyo wathu.

15 Tichititseni kuti tisangalale kwa masiku ofanana ndi masiku amene mwatisautsa,+

Kwa zaka zofanana ndi zaka zimene takumana ndi masoka.+

16 Atumiki anu aone ntchito zanu,

Ndipo ana awo aone ulemerero wanu.+

17 Yehova Mulungu wathu atikomere mtima.

Chititsani kuti ntchito ya manja athu iyende bwino.*

Inde, chititsani kuti ntchito ya manja athu iyende bwino.*+

91 Aliyense amene akukhala mʼmalo obisika a Wamʼmwambamwamba+

Adzakhala mumthunzi wa Wamphamvuyonse.+

 2 Ndidzauza Yehova kuti: “Inu ndinu malo anga othawirako komanso malo anga achitetezo,+

Mulungu wanga amene ndimamukhulupirira.”+

 3 Chifukwa iye adzakupulumutsa mumsampha wa wosaka mbalame,

Komanso ku mliri wowononga.

 4 Adzakuphimba ndi mapiko ake,

Ndipo udzathawira pansi pa mapiko ake.*+

Kukhulupirika kwake+ kudzakhala chishango chako chachikulu+ komanso khoma lokuteteza.

 5 Usiku sudzaopa choopsa chilichonse,+

Kapena muvi woponyedwa masana,+

 6 Sudzaopa mliri umene umafalikira mumdima,

Kapena chiwonongeko chimene chimachitika masana.

 7 Anthu 1,000 adzagwa pambali pako,

Ndipo anthu 10,000 adzagwa kudzanja lako lamanja.

Koma palibe choipa chilichonse chimene chidzakuchitikire.+

 8 Maso ako adzaona zimenezi zikuchitika,

Pamene anthu oipa akulandira chilango.*

 9 Popeza wanena kuti: “Yehova ndi malo anga othawirako,”

Wapanga Wamʼmwambamwamba kuti akhale malo ako okhalamo.+

10 Palibe tsoka limene lidzakugwere,+

Ndipo palibe mliri umene udzayandikire tenti yako.

11 Chifukwa adzalamula angelo ake+ zokhudza iwe,

Kuti akuteteze mʼnjira zako zonse.+

12 Iwo adzakunyamula mʼmanja mwawo,+

Kuti phazi lako lisawombe mwala.+

13 Udzapondaponda mkango wamphamvu ndi njoka ya mamba,

Ndipo udzapondaponda mkango wamphamvu kwambiri komanso chinjoka chachikulu.+

14 Mulungu ananena kuti: “Popeza amandikonda,* ine ndidzamupulumutsa.+

Ndidzamuteteza chifukwa akudziwa* dzina langa.+

15 Adzandiitana ndipo ndidzamuyankha.+

Ndidzakhala naye pa nthawi ya mavuto.+

Ndidzamupulumutsa komanso kumupatsa ulemerero.

16 Ndidzamupatsa moyo wautali,+

Ndipo ndidzamuchititsa kuti aone mmene ndidzamupulumutsire.”*+

Nyimbo ndi Salimo la pa tsiku la Sabata.

92 Ndi bwino kuyamika inu Yehova,+

Ndiponso kuimba nyimbo zotamanda dzina lanu, inu Wamʼmwambamwamba.

 2 Ndi bwino kulengeza chikondi chanu chokhulupirika+ mʼmawa,

Ndi kukhulupirika kwanu usiku,

 3 Pogwiritsa ntchito choimbira cha zingwe 10 ndi choimbira cha zingwe zitatu,

Komanso nyimbo zosangalatsa zoimbidwa ndi zeze.+

 4 Inu Yehova mwachititsa kuti ndisangalale chifukwa cha zochita zanu.

Ndimafuula mosangalala chifukwa cha ntchito za manja anu.

 5 Ntchito zanu ndi zazikulu kwambiri inu Yehova!+

Maganizo anu ndi ozama kwambiri.+

 6 Munthu wopanda nzeru sangadziwe zimenezi,

Ndipo munthu wopusa sangamvetse izi:+

 7 Anthu oipa akaphuka ngati msipu

Ndipo anthu onse ochita zoipa zinthu zikamawayendera bwino,

Zimatero kuti awonongedwe kwamuyaya.+

 8 Koma inu Yehova, ndinu wokwezeka mpaka kalekale.

 9 Onani adani anu atagonjetsedwa, inu Yehova,

Onani mmene adani anu adzathere,

Onse ochita zoipa adzamwazikana.+

10 Koma inu mudzawonjezera mphamvu* zanga kuti zikhale ngati za ngʼombe yamphongo yamʼtchire.

Khungu langa ndidzalidzoza mafuta abwino kwambiri.+

11 Maso anga adzaona adani anga atagonja.+

Makutu anga adzamva za kugwa kwa anthu oipa amene amandiukira.

12 Koma olungama zinthu zidzawayendera bwino ngati mtengo wa kanjedza

Ndipo adzakula kwambiri ngati mtengo wa mkungudza wa ku Lebanoni.+

13 Iwo anadzalidwa mʼnyumba ya Yehova,

Zinthu zikuwayendera bwino mʼmabwalo a Mulungu wathu.+

14 Ngakhale atakalamba* zinthu zidzapitirizabe kuwayendera bwino.+

Adzakhalabe amphamvu* ndi athanzi,+

15 Ndipo adzalengeza kuti Yehova ndi wolungama.

Iye ndi Thanthwe langa,+ ndipo sachita zosalungama.

93 Yehova wakhala Mfumu!+

Iye wavala ulemerero.

Yehova wavala mphamvu

Wazivala ngati lamba wamʼchiuno.

Dziko lapansi lakhazikika,

Moti silingasunthidwe.*

 2 Mpando wanu wachifumu unakhazikika kalekale.+

Munakhalako kuyambira kalekale.+

 3 Inu Yehova, mitsinje yasefukira,

Mitsinje yasefukira ndipo ikuchita mkokomo.

Mitsinje ikupitiriza kusefukira komanso kuchita mkokomo.

 4 Ulemerero wa Yehova ndi waukulu kumwamba,

Kuposa mkokomo wa madzi ambiri,+

Ndi wamphamvu kuposa mafunde amphamvu amʼnyanja.+

 5 Zikumbutso zanu ndi zodalirika kwambiri.+

Inu Yehova, nyumba yanu ndi yokongola komanso yoyera+ nthawi zonse.

94 Inu Yehova, Mulungu amene amabwezera anthu oipa,+

Inu Mulungu amene amabwezera anthu oipa, onetsani kuwala kwanu!

 2 Nyamukani, inu Woweruza dziko lapansi.+

Perekani chilango kwa anthu onyada chifukwa cha zimene achita.+

 3 Inu Yehova, kodi anthu oipa adzapitiriza kusangalala mpaka liti?

Adzapitiriza kukondwera mpaka liti?+

 4 Zolankhula zawo zimasonyeza kuti ndi opusa komanso onyada.

Anthu onse ochita zoipa amalankhula modzitama.

 5 Iwo amaphwanya anthu anu, inu Yehova,+

Ndipo amapondereza cholowa chanu.

 6 Amapha mkazi wamasiye komanso mlendo,

Ndipo amaphanso ana amasiye.

 7 Iwo amanena kuti: “Ya sakuona,+

Ndipo Mulungu wa Yakobo sakudziwa zimene zikuchitika.”+

 8 Zindikirani izi, anthu opanda nzeru inu.

Anthu opusa inu, kodi mudzasonyeza liti kuti ndinu ozindikira?+

 9 Kodi amene anapanga* makutu, sangamve?

Kodi amene anapanga maso, sangaone?+

10 Kodi amene amalangiza mitundu ya anthu, sangathe kudzudzula?+

Iye ndi amene amaphunzitsa anthu kuti akhale ozindikira.+

11 Yehova amadziwa maganizo a anthu,

Amadziwa kuti ali ngati mpweya.+

12 Wosangalala ndi munthu amene inu Ya, mumamulangiza,+

Amene inu mumamuphunzitsa chilamulo chanu,+

13 Kuti mumupatse mtendere pa nthawi ya masoka,

Mpaka dzenje la oipa litakumbidwa.+

14 Yehova sadzataya anthu ake,+

Kapena kusiya cholowa chake.+

15 Chifukwa oweruza adzayambiranso kupereka zigamulo zachilungamo,

Ndipo onse owongoka mtima adzazitsatira.

16 Ndi ndani amene adzanditeteze kwa oipa?

Ndi ndani amene adzakhale kumbali yanga polimbana ndi anthu ochita zoipa?

17 Yehova akanapanda kundithandiza,

Bwenzi nditafa* kalekale.+

18 Pamene ndinanena kuti: “Phazi langa likuterereka,”

Chikondi chanu chokhulupirika, inu Yehova, chinapitiriza kundithandiza.+

19 Nkhawa zitandichulukira,*

Munanditonthoza komanso kundisangalatsa.*+

20 Kodi inu mungagwirizane ndi olamulira achinyengo

Pamene akuyambitsa mavuto pogwiritsa ntchito malamulo?+

21 Iwo amaukira mwankhanza munthu wolungama,*+

Ndipo munthu wosalakwa amamuweruza kuti akuyenera kuphedwa.*+

22 Koma Yehova adzakhala malo anga othawirako otetezeka,*

Mulungu wanga ndi thanthwe langa lothawirako.+

23 Iye adzachititsa kuti zoipa zimene akuchita zibwerere kwa iwo.+

Iye adzawawononga* pogwiritsa ntchito zoipa zawo zomwe.

Yehova Mulungu wathu adzawawononga.*+

95 Bwerani, tiyeni tifuule kwa Yehova mosangalala!

Tiyeni tifuule mosangalala ndipo titamande Thanthwe la chipulumutso chathu.+

 2 Tiyeni tikaonekere pamaso pake moyamikira.+

Tiyeni timuimbire nyimbo zomutamanda ndipo tifuule mosangalala.

 3 Chifukwa Yehova ndi Mulungu wamkulu,

Iye ndi Mfumu yaikulu kuposa milungu ina yonse.+

 4 Malo ozama kwambiri a dziko lapansi ali mʼmanja mwake,

Mapiri aatali nawonso ndi ake.+

 5 Nyanja imene iye anapanga ndi yake,+

Ndipo manja ake anapanganso mtunda.+

 6 Bwerani, tiyeni timulambire komanso kumugwadira.

Tiyeni tigwade pamaso pa Yehova amene anatipanga.+

 7 Chifukwa iye ndi Mulungu wathu

Ndipo ife ndi anthu amene iye akuweta,

Nkhosa zimene akuzisamalira.*+

Lero anthu inu mukamvera mawu ake,+

 8 Musaumitse mitima yanu ngati mmene makolo anu anachitira ku Meriba,*+

Ngati mmene anachitira ku Masa* mʼchipululu,+

 9 Pamene makolo anu anandiyesa.+

Iwo anatsutsana ndi ine ngakhale kuti anaona ntchito zanga.+

10 Kwa zaka 40, mʼbadwo umenewo unkandinyansa ndipo ndinati:

“Awa ndi anthu amene mitima yawo imasochera nthawi zonse,

Njira zanga sakuzidziwa.”

11 Choncho ndinalumbira nditakwiya kuti:

“Sadzalowa mumpumulo wanga.”+

96 Imbirani Yehova nyimbo yatsopano.+

Dziko lonse lapansi liimbire Yehova.+

 2 Imbirani Yehova, tamandani dzina lake.

Tsiku ndi tsiku muzilengeza uthenga wabwino wa chipulumutso chake.+

 3 Lengezani ulemerero wake pakati pa anthu a mitundu ina,

Lengezani ntchito zake zodabwitsa pakati pa mitundu yonse ya anthu.+

 4 Yehova ndi wamkulu komanso woyenera kutamandidwa kwambiri.

Iye ndi wochititsa mantha kwambiri kuposa milungu ina yonse.

 5 Milungu yonse ya anthu a mitundu ina ndi milungu yopanda pake,+

Koma Yehova ndi amene anapanga kumwamba.+

 6 Pamene amakhala pali ulemu ndi ulemerero.+

Mphamvu ndi kukongola zili mʼnyumba yake yopatulika.+

 7 Mʼpatseni Yehova zimene akuyenera kulandira, inu mabanja a mitundu ya anthu,

Mʼpatseni Yehova zimene akuyenera kulandira chifukwa cha ulemerero ndi mphamvu zake.+

 8 Mʼpatseni Yehova ulemerero woyenera dzina lake.+

Bweretsani mphatso ndi kulowa mʼmabwalo ake.

 9 Gwadirani* Yehova mutavala zovala zokongola komanso zopatulika.*

Dziko lonse lapansi linjenjemere pamaso pake.

10 Lengezani pakati pa anthu a mitundu ina kuti: “Yehova wakhala Mfumu.+

Dziko lapansi lakhazikika moti silingasunthidwe.*

Iye adzaweruza mitundu ya anthu mwachilungamo.”*+

11 Kumwamba kukondwere ndipo dziko lapansi lisangalale.

Nyanja ichite mkokomo ndi zonse zimene zili mmenemo.+

12 Mtunda ndi zonse zimene zili pamenepo zikondwere.+

Pa nthawi imodzimodziyo, mitengo yonse yamʼnkhalango ifuule mosangalala+

13 Pamaso pa Yehova, chifukwa iye akubwera,*

Iye akubwera kudzaweruza dziko lapansi.

Adzaweruza anthu okhala padziko lapansi mwachilungamo+

Ndipo adzaweruza mitundu ya anthu mokhulupirika.+

97 Yehova wakhala Mfumu!+

Dziko lapansi lisangalale.+

Zilumba zambiri zikondwere.+

 2 Mitambo ndi mdima wandiweyani zamuzungulira.+

Maziko a mpando wake wachifumu ndi chilungamo komanso chiweruzo cholungama.+

 3 Moto umachoka kwa iye+

Nʼkupsereza adani ake omuzungulira.+

 4 Kungʼanima kwa mphezi zake kumaunika dziko.

Dziko lapansi limaona zimenezi ndipo limanjenjemera.+

 5 Mapiri amasungunuka ngati phula pamaso pa Yehova,+

Pamaso pa Ambuye wa dziko lonse lapansi.

 6 Kumwamba kumalengeza za chilungamo chake,

Ndipo mitundu yonse ya anthu imaona ulemerero wake.+

 7 Onse amene akutumikira chifaniziro chilichonse achite manyazi,+

Amene amadzitama chifukwa cha milungu yawo yopanda pake.+

Muweramireni,* inu milungu yonse.+

 8 Ziyoni wamva ndipo akusangalala,+

Matauni* a ku Yuda akukondwera

Chifukwa cha zigamulo zanu, inu Yehova.+

 9 Chifukwa inu Yehova, ndinu Wamʼmwambamwamba woyenera kulamulira dziko lonse lapansi.

Ndinu wokwezeka kwambiri kuposa milungu ina yonse.+

10 Inu amene mumakonda Yehova, muzidana ndi zoipa.+

Iye amateteza moyo wa anthu ake okhulupirika.+

Amawapulumutsa mʼmanja mwa* oipa.+

11 Kuwala kwaunikira olungama+

Ndipo owongoka mtima akusangalala.

12 Sangalalani chifukwa cha Yehova, olungama inu,

Ndipo yamikirani dzina lake loyera.*

Nyimbo.

98 Imbirani Yehova nyimbo yatsopano,+

Chifukwa wachita zinthu zodabwitsa.+

Dzanja lake lamanja, mkono wake woyera, wabweretsa chipulumutso.*+

 2 Yehova wachititsa kuti chipulumutso chake chidziwike.+

Wachititsa kuti anthu a mitundu yonse aone chilungamo chake.+

 3 Iye wakumbukira chikondi chake chokhulupirika komanso kukhulupirika kumene analonjeza nyumba ya Isiraeli.+

Anthu onse padziko lapansi aona mmene Mulungu wathu wapulumutsira anthu ake.*+

 4 Dziko lonse lapansi lifuulire Yehova mosangalala chifukwa wapambana.

Kondwerani ndipo fuulani mosangalala komanso imbani nyimbo zomutamanda.+

 5 Imbirani Yehova nyimbo zomutamanda pogwiritsa ntchito zeze,

Mutamandeni ndi nyimbo zosangalatsa pogwiritsa ntchito zeze.

 6 Fuulani mosangalala pamaso pa Mfumu Yehova,

Poimba malipenga komanso lipenga la nyanga ya nkhosa chifukwa wapambana.+

 7 Nyanja ichite mkokomo ndi zonse zimene zili mmenemo,

Chimodzimodzinso dziko lapansi komanso amene akukhala mmenemo.

 8 Mitsinje iwombe mʼmanja,

Mapiri afuule pamodzi mosangalala+

 9 Pamaso pa Yehova chifukwa iye akubwera kudzaweruza dziko lapansi.

Adzaweruza anthu okhala padziko lapansi mwachilungamo+

Ndipo adzaweruza mitundu ya anthu mwachilungamo.+

99 Yehova wakhala Mfumu.+ Mitundu ya anthu injenjemere.

Iye wakhala pampando wachifumu pamwamba* pa akerubi.+ Dziko lapansi ligwedezeke.

 2 Yehova ndi wamkulu mu Ziyoni,

Ndipo iye ali pamwamba pa mitundu yonse ya anthu.+

 3 Iwo atamande dzina lanu lalikulu,+

Chifukwa ndi lochititsa mantha komanso loyera.

 4 Iye ndi mfumu yamphamvu imene imakonda chilungamo.+

Nthawi zonse mumaonetsetsa kuti chilungamo chachitika.

Mwabweretsa chiweruzo cholungama komanso chilungamo+ pakati pa ana a Yakobo.

 5 Kwezani Yehova Mulungu wathu+ ndipo mugwadireni* pachopondapo mapazi ake.+

Iye ndi woyera.+

 6 Mose ndi Aroni anali mʼgulu la ansembe ake,+

Ndipo Samueli anali mʼgulu la anthu amene ankaitana pa dzina lake.+

Iwo ankaitana Yehova,

Ndipo iye ankawayankha.+

 7 Mulungu ankalankhula nawo kuchokera mʼchipilala cha mtambo.+

Iwo anasunga zikumbutso zake ndi malamulo amene anawapatsa.+

 8 Inu Yehova Mulungu wathu munawayankha.+

Inu ndi Mulungu amene munawakhululukira,+

Koma munawalanga chifukwa cha machimo awo.+

 9 Kwezani Yehova Mulungu wathu+

Ndipo mugwadireni* paphiri lake loyera,+

Chifukwa Yehova Mulungu wathu ndi woyera.+

Nyimbo yoyamikira.

100 Dziko lonse lapansi lifuulire Yehova mosangalala chifukwa wapambana.+

 2 Tumikirani Yehova mokondwera.+

Bwerani kwa iye mukufuula mosangalala.

 3 Dziwani* kuti Yehova ndi Mulungu.+

Iye ndi amene anatipanga, ndipo ndife ake.+

Ndife anthu ake komanso nkhosa zimene akuweta.+

 4 Lowani pamageti ake mukumuyamikira,+

Lowani mʼmabwalo ake mukumutamanda.+

Muyamikeni, tamandani dzina lake.+

 5 Chifukwa Yehova ndi wabwino.+

Chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale,

Ndipo kukhulupirika kwake kudzakhalapo ku mibadwo yonse.+

Nyimbo ndi Salimo la Davide.

101 Ndidzaimba za chikondi chokhulupirika komanso chilungamo chanu.

Inu Yehova, ndidzakuimbirani nyimbo zokutamandani.

 2 Ndidzachita zinthu mwanzeru komanso mosalakwitsa kanthu.*

Kodi mudzandithandiza liti?

Ndidzayenda mʼnyumba yanga ndi mtima wokhulupirika.+

 3 Sindidzayangʼana chinthu chilichonse choipa.*

Ndimadana ndi zochita za anthu amene asiya kuchita zinthu zabwino.+

Sindidzalola kuti zochita zawozo zindikhudze.

 4 Aliyense wopotoka maganizo, ali kutali ndi ine.

Sindidzalola* kuchita zinthu zoipa.

 5 Aliyense wonenera mnzake miseche,+

Ndidzamukhalitsa chete.*

Aliyense amene ali ndi mtima wonyada komanso wodzikweza,

Sindidzamulekerera.

 6 Ndidzayangʼana anthu okhulupirika kwa inu padziko lapansi,

Kuti azikhala ndi ine.

Amene akuyenda mosalakwitsa kanthu* adzanditumikira.

 7 Mʼnyumba yanga simudzakhala munthu wachinyengo,

Ndipo wabodza aliyense sadzaima pamaso panga.

 8 Mʼmawa uliwonse ndidzawononga* oipa onse apadziko lapansi,

Ndidzapha onse ochita zoipa nʼkuwachotsa mumzinda wa Yehova.+

Pemphero la munthu woponderezedwa pamene ali pamavuto* ndipo akutula nkhawa zake kwa Yehova.+

102 Inu Yehova, imvani pemphero langa.+

Imvani kufuula kwanga kopempha thandizo.+

 2 Musandibisire nkhope yanu pamene ndili pamavuto aakulu.+

Tcherani khutu lanu kwa ine.*

Ndiyankheni mofulumira pamene ndikuitana.+

 3 Chifukwa masiku a moyo wanga akuzimiririka ngati utsi,

Ndipo mafupa anga akutentha kwambiri ngati ngʼanjo.+

 4 Mtima wanga wakhala ngati udzu umene wawauka nʼkuuma,+

Chifukwa sindikulakalaka kudya chakudya.

 5 Chifukwa chakuti ndikubuula mokweza mawu,+

Ndangotsala mafupa okhaokha.+

 6 Ndikufanana ndi mbalame yamʼchipululu yotchedwa vuwo.

Ndakhala ngati nkhwezule yamʼmabwinja.

 7 Ndikusowa tulo.

Ndili ngati mbalame imene ili yokhayokha padenga.+

 8 Tsiku lonse adani anga amandinyoza.+

Anthu amene amanditonza amagwiritsa ntchito dzina langa potemberera ena.

 9 Ndikudya phulusa ngati chakudya,+

Ndipo zakumwa zanga ndi zosakanikirana ndi misozi.+

10 Izi zili choncho chifukwa cha mkwiyo ndi ukali wanu,

Popeza munandikweza mʼmwamba kuti munditaye.

11 Masiku a moyo wanga ali ngati chithunzithunzi chimene chimazimiririka,+

Ndipo ndafota ngati udzu.+

12 Koma inu Yehova, mudzakhalapobe kwamuyaya,+

Dzina lanu lidzakhalapobe* ku mibadwo yonse.+

13 Ndithudi inu mudzanyamuka nʼkusonyeza Ziyoni chifundo,+

Chifukwa imeneyi ndi nthawi yoti mumusonyeze kukoma mtima kwanu.+

Nthawi yoikidwiratu yakwana.+

14 Atumiki anu amasangalala ndi miyala ya mpanda wake,+

Ndipo amakonda ngakhale fumbi lake.+

15 Mitundu ya anthu idzaopa dzina lanu, inu Yehova,

Ndipo mafumu onse apadziko lapansi adzaopa ulemerero wanu.+

16 Chifukwa Yehova adzamanganso Ziyoni.+

Iye adzaonekera mu ulemerero wake.+

17 Adzamvetsera pemphero la anthu osauka.+

Iye sadzapeputsa pemphero lawo.+

18 Zimenezi zalembedwera mʼbadwo wamʼtsogolo,+

Kuti anthu amene akubwera mʼtsogolo* adzatamande Ya.

19 Iye amayangʼana pansi ali pamalo ake apamwamba omwe ndi oyera,+

Yehova amayangʼana dziko lapansi ali kumwamba,

20 Kuti amve kuusa moyo kwa mkaidi,+

Komanso kuti amasule anthu amene aweruzidwa kuti akaphedwe.+

21 Wachita izi kuti dzina la Yehova lilengezedwe mʼZiyoni+

Komanso kuti atamandidwe mu Yerusalemu,

22 Pamene mitundu ya anthu komanso maufumu

Adzasonkhana pamodzi kuti atumikire Yehova.+

23 Anandilanda mphamvu zanga nthawi yake isanakwane.

Anafupikitsa masiku a moyo wanga.

24 Ine ndinati: “Inu Mulungu wanga,

Musachotse moyo wanga ndisanakalambe,

Inu amene mudzakhalapo ku mibadwo yonse.+

25 Munakhazikitsa maziko a dziko lapansi kalekale,

Ndipo kumwamba ndi ntchito ya manja anu.+

26 Zimenezi zidzatha, koma inu mudzakhalapobe.

Mofanana ndi chovala, zonsezi zidzatha.

Mofanana ndi zovala zimene zatha, mudzapezerapo zina ndipo nazonso zidzatha.

27 Koma inu simusintha ndipo mudzakhalapo mpaka kalekale.+

28 Ana a atumiki anu adzakhala motetezeka,

Ndipo ana awo adzakhala motetezeka pamaso panu.”+

Salimo la Davide.

103 Moyo wanga utamande Yehova.

Chilichonse cha mkati mwanga, chitamande dzina lake loyera.

 2 Moyo wanga utamande Yehova,

Ndisaiwale zinthu zonse zimene wachita.+

 3 Iye amakukhululukira zolakwa zako zonse+

Ndipo amachiritsa matenda ako onse.+

 4 Iye amawombola moyo wako kudzenje,*+

Ndipo amakuveka chikondi chake chokhulupirika komanso chifundo ngati chisoti chachifumu.+

 5 Iye amakupatsa zinthu zabwino+ nthawi yonse ya moyo wako, zimene umakhutira nazo,

Kuti ukhalebe wachinyamata ndi wamphamvu ngati chiwombankhanga.+

 6 Yehova amachita chilungamo+ kwa anthu onse oponderezedwa

Ndipo amaweruza milandu yawo mwachilungamo.+

 7 Anadziwitsa Mose njira zake,+

Ndipo ana a Isiraeli anawadziwitsa zochita zake.+

 8 Yehova ndi wachifundo ndi wokoma mtima,*+

Wosakwiya msanga ndiponso wachikondi chokhulupirika chochuluka.*+

 9 Iye sadzakhalira kutipezera zifukwa nthawi zonse,+

Kapena kutisungira mkwiyo mpaka kalekale.+

10 Sanatichitire mogwirizana ndi machimo athu,+

Kapena kutipatsa chilango chogwirizana ndi zolakwa zathu.+

11 Mofanana ndi mmene kumwamba kulili pamwamba kwambiri kuposa dziko lapansi,

Chikondi chokhulupirika chimene amasonyeza anthu amene amamuopa ndi chachikulu kwambiri.+

12 Mofanana ndi mmene kotulukira dzuwa kwatalikirana ndi kolowera dzuwa,

Mulungu waikanso zolakwa zathu kutali ndi ife.+

13 Mofanana ndi bambo amene amasonyeza chifundo kwa ana ake,

Yehova wasonyezanso chifundo kwa anthu amene amamuopa.+

14 Chifukwa iye akudziwa bwino mmene anatipangira,+

Amakumbukira kuti ndife fumbi.+

15 Masiku a moyo wa munthu ali ngati masiku a udzu.+

Iye amaphuka ngati duwa lakutchire.+

16 Koma mphepo ikawomba limafa,

Ndipo zimangokhala ngati panalibepo.*

17 Koma Yehova adzapitiriza kusonyeza chikondi chake chokhulupirika mpaka kalekale

Kwa anthu amene amamuopa,+

Ndipo adzapitiriza kusonyeza chilungamo chake kwa ana a ana awo.+

18 Adzapitiriza kuchita zimenezi kwa anthu amene amasunga pangano lake,+

Ndi kwa anthu amene amatsatira malamulo ake mosamala.

19 Yehova wakhazikitsa mpando wake wachifumu kumwamba.+

Ndipo ufumu wake ukulamulira chilichonse.+

20 Tamandani Yehova, inu angelo ake onse+ amphamvu,

Amene amamvera mawu ake komanso kuchita zimene wanena.+

21 Tamandani Yehova, inu magulu ake onse a angelo,+

Atumiki ake amene amachita chifuniro chake.+

22 Tamandani Yehova, inu ntchito zake zonse,

Mʼmalo onse amene iye akulamulira.

Moyo wanga wonse utamande Yehova.

104 Moyo wanga utamande Yehova.+

Inu Yehova Mulungu wanga, ndinu wamkulu kwambiri.+

Mwavala ulemu ndi ulemerero.+

 2 Mwadzifunditsa kuwala+ ngati chofunda,

Mwatambasula kumwamba ngati nsalu yopangira tenti.+

 3 Iye amamanga zipinda zake pamadzi amumlengalenga+ pogwiritsa ntchito matabwa,

Amapanga mitambo kukhala galeta lake,+

Amayenda pamapiko a mphepo.+

 4 Iye amachititsa kuti angelo ake akhale amphamvu,*

Amachititsa atumiki ake kuti akhale moto wopsereza.+

 5 Iye wakhazikitsa dziko lapansi pamaziko ake.+

Silidzasunthidwa pamalo ake* mpaka kalekale.+

 6 Munaliphimba ndi madzi ozama ngati kuti mwaliphimba ndi nsalu.+

Madziwo anakwera kupitirira mapiri.

 7 Chifukwa cha kudzudzula kwanu, madziwo anathawa.+

Atamva mabingu anu anayamba kuthawa mopanikizika kwambiri

 8 Kupita kumalo amene munawakonzera.

Mapiri anakwera+ ndipo zigwa zinatsika.

 9 Munawaikira malire kuti asapitirire malirewo,+

Kuti asadzamizenso dziko lapansi.

10 Amatulutsa madzi mu akasupe kuti apite mʼzigwa*

Ndipo madziwo amadutsa pakati pa mapiri.

11 Akasupewo amapereka madzi kwa zilombo zonse zakutchire.

Abulu amʼtchire amapha ludzu lawo mmenemo.

12 Mbalame zamumlengalenga zimamanga zisa zawo pafupi ndi akasupewo,

Ndipo zimaimba mʼmitengo ya masamba ambiri.

13 Mulungu amathirira mapiri kuchokera mʼzipinda zake zamʼmwamba.+

Dziko lapansi ladzaza ndi zipatso za ntchito zanu.+

14 Amameretsa msipu kuti ngʼombe zidye,

Ndipo amameretsa mbewu kuti anthu agwiritse ntchito.+

Amachita zimenezi kuti chakudya chituluke mʼnthaka

15 Komanso kuti mutuluke vinyo amene amasangalatsa mtima wa munthu,+

Mafuta amene amachititsa kuti nkhope ya munthu isalale,

Ndiponso chakudya chimene chimapereka mphamvu kwa munthu.*+

16 Mitengo ya Yehova imalandira madzi okwanira,

Mikungudza ya ku Lebanoni imene iye anadzala,

17 Mbalame zimamanga zisa zawo mmenemo.

Nyumba ya dokowe+ imakhala mʼmitengo ya junipa.*

18 Mʼmapiri aatali ndi mmene mumakhala mbuzi zamʼmapiri.+

Ndipo mʼmapanga ndi mmene mbira zimathawiramo.+

19 Wapanga mwezi kuti uzisonyeza nthawi yoikidwiratu.

Dzuwa limadziwa bwino nthawi yoyenera kulowa.+

20 Mumabweretsa mdima ndipo usiku umayamba,+

Nthawi imene nyama zonse zakutchire zimayendayenda.

21 Mikango yamphamvu* imabangula pofunafuna nyama,+

Ndipo imapempha chakudya kwa Mulungu.+

22 Dzuwa likatuluka,

Nyamazi zimachoka ndipo zimakagona mʼmalo amene zimakhala.

23 Munthu amapita kuntchito yake,

Ndipo amagwira ntchito mpaka madzulo.

24 Ntchito zanu ndi zochuluka, inu Yehova!+

Zonsezo munazipanga mwanzeru.+

Dziko lapansi ladzaza ndi zinthu zimene munapanga.

25 Pali nyanja, yomwe ndi yakuya komanso yaikulu kwambiri,

Mmene muli zamoyo zosawerengeka, zazikulu ndi zazingʼono zomwe.+

26 Sitima zimayenda mmenemo,

Ndipo Leviyatani*+ munamupanga kuti azisewera mmenemo.

27 Zonsezi zimayembekezera inu

Kuti muzipatse chakudya pa nyengo yake.+

28 Zimasonkhanitsa zimene mwazipatsa.+

Mukatambasula dzanja lanu, zimakhutira ndi zinthu zabwino.+

29 Mukabisa nkhope yanu, zimasokonezeka.

Mukachotsa mzimu wawo,* zimafa ndipo zimabwerera kufumbi.+

30 Mukatumiza mzimu wanu zimalengedwa,+

Ndipo mumachititsa kuti zinthu zonse padziko lapansi zikhale zatsopano.

31 Ulemerero wa Yehova udzakhalapobe mpaka kalekale.

Yehova adzakondwera ndi ntchito zake.+

32 Amayangʼana dziko lapansi ndipo limanjenjemera.

Amagwira mapiri ndipo amafuka utsi.+

33 Ndidzaimbira Yehova+ moyo wanga wonse.

Ndidzaimba nyimbo zotamanda Mulungu wanga nthawi yonse ya moyo wanga.+

34 Zimene ndimaganiza zizimusangalatsa.

Ine ndidzasangalala chifukwa cha Yehova.

35 Ochimwa adzachotsedwa padziko lapansi,

Ndipo oipa sadzakhalaponso.+

Moyo wanga utamande Yehova. Tamandani Ya!*

105 Yamikani Yehova,+ itanani pa dzina lake,

Dziwitsani mitundu ya anthu ntchito zake.+

 2 Muimbireni, muimbireni nyimbo zomutamanda,

Ganizirani mozama* ntchito zake zonse zodabwitsa.+

 3 Nyadirani dzina lake loyera.+

Mitima ya anthu ofunafuna Yehova isangalale.+

 4 Funafunani Yehova+ ndipo muzidalira mphamvu zake.

Nthawi zonse muzimupempha kuti akuthandizeni.*

 5 Kumbukirani ntchito zodabwitsa zimene wachita,

Kumbukirani zozizwitsa zake ndi ziweruzo zimene wapereka,+

 6 Inu mbadwa* za Abulahamu mtumiki wake,+

Inu ana a Yakobo, osankhidwa ake.+

 7 Iye ndi Yehova Mulungu wathu.+

Ziweruzo zake zili padziko lonse lapansi.+

 8 Amakumbukira pangano lake mpaka kalekale,+

Lonjezo limene anapereka* ku mibadwo 1,000.+

 9 Wakumbukira pangano limene anapangana ndi Abulahamu,+

Komanso lumbiro limene analumbira kwa Isaki,+

10 Limene analikhazikitsa monga lamulo kwa Yakobo,

Komanso monga pangano lokhalapo mpaka kalekale kwa Isiraeli,

11 Pamene anati, “Ndidzakupatsa dziko la Kanani+

Kuti likhale cholowa chako.”+

12 Pamene ananena zimenezi, nʼkuti iwo ali ochepa.+

Nʼkuti ali ochepa kwambiri komanso ali alendo mʼdzikolo.+

13 Iwo ankayendayenda kuchokera ku mtundu wina kupita ku mtundu wina,

Komanso kuchokera mu ufumu wina kupita kwa anthu a mtundu wina.+

14 Mulungu sanalole kuti munthu aliyense awapondereze,+

Koma anadzudzula mafumu chifukwa cha iwo.+

15 Iye anati: “Musakhudze odzozedwa anga,

Ndipo aneneri anga musawachitire choipa chilichonse.”+

16 Iye anagwetsa njala yaikulu mʼdzikomo,+

Iye anachititsa kuti asathenso kupeza chakudya.*

17 Mulungu anatsogoza Yosefe,

Munthu amene anagulitsidwa kuti akhale kapolo.+

18 Kumeneko anamanga* mapazi ake mʼmatangadza,+

Khosi lake analiika mʼzitsulo

19 Mpaka nthawi imene zimene Mulungu ananena zinakwaniritsidwa,+

Mawu a Yehova ndi amene anamuyenga.

20 Mfumu inalamula kuti amutulutse mʼndende,+

Wolamulira mitundu ya anthu anatulutsa Yosefe mʼndende.

21 Anamupatsa udindo woyangʼanira banja lake

Komanso woyangʼanira chuma chake chonse.+

22 Anamupatsa mphamvu zolamulira* akalonga ake mmene akufunira

Komanso kuti akuluakulu aziwaphunzitsa zinthu za nzeru.+

23 Kenako Isiraeli anapita ku Iguputo+

Ndipo Yakobo anakhala monga mlendo mʼdziko la Hamu.

24 Mulungu anachititsa kuti anthu ake aberekane kwambiri,+

Iye anawachititsa kuti akhale amphamvu kwambiri kuposa adani awo.+

25 Analola adaniwo kuti asinthe mitima yawo nʼkuyamba kudana ndi anthu ake,

Komanso kukonzera chiwembu atumiki akewo.+

26 Ndiyeno anatumiza Mose mtumiki wake,+

Ndi Aroni+ amene anamusankha.

27 Iwowa anachita zizindikiro za Mulungu pamaso pa Aiguputo,

Anachita zodabwitsa zake mʼdziko la Hamu.+

28 Mulungu anachititsa kuti mʼdziko la Iguputo mukhale mdima.+

Iwo* sanapandukire mawu ake.

29 Anasandutsa madzi a Aiguputo kukhala magazi,

Ndipo anapha nsomba zawo.+

30 Mʼdziko lawo munadzaza achule,+

Ngakhalenso mʼzipinda za mafumu awo.

31 Analamula kuti pagwe ntchentche zoluma,

Komanso tizilombo touluka toyamwa magazi,* mʼmadera awo onse.+

32 Anawagwetsera matalala mʼmalo mwa mvula,

Anagwetsa mphezi* mʼdziko lawo.+

33 Anawononga mitengo yawo ya mpesa ndi ya mkuyu

Ndipo anakhadzula mitengo mʼdziko lawo.

34 Analamula kuti pagwe dzombe,

Dzombe lingʼonolingʼono losawerengeka.+

35 Dzombelo linadya zomera zonse mʼdziko lawo,

Linadyanso mbewu zonse zamʼmunda mwawo.

36 Kenako Mulungu anapha mwana aliyense woyamba kubadwa mʼdziko lawo,+

Chiyambi cha mphamvu zawo zobereka.

37 Anatulutsa anthu ake atatenga siliva ndi golide.+

Ndipo pakati pa mafuko ake panalibe amene anapunthwa panjira.

38 Aiguputo anasangalala Aisiraeli atatuluka mʼdzikolo,

Chifukwa ankawaopa kwambiri.+

39 Mulungu anatumiza mtambo kuti uwateteze+

Komanso moto kuti uziwaunikira usiku.+

40 Anapempha nyama ndipo anawapatsa zinziri,+

Ankawadyetsa chakudya chochokera kumwamba.+

41 Anatsegula thanthwe ndipo panatuluka madzi ambiri.+

Madziwo anayenda ngati mtsinje kudutsa mʼchipululu.+

42 Chifukwa iye anakumbukira lonjezo lake loyera limene analonjeza mtumiki wake Abulahamu.+

43 Choncho Mulungu anatulutsa anthu ake mʼdzikomo anthuwo akusangalala,+

Anatulutsa osankhidwa ake akufuula mokondwera.

44 Anawapatsa mayiko a anthu a mitundu ina,+

Anatenga zinthu zimene mitundu ina ya anthu inapeza itagwira ntchito mwakhama,+

45 Anachita zimenezi kuti asunge malangizo ake,+

Komanso kusunga malamulo ake.

Tamandani Ya!*

106 Tamandani Ya!*

Yamikani Yehova chifukwa iye ndi wabwino.+

Chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale.+

 2 Ndi ndani amene anganene za ntchito zonse zazikulu za Yehova,

Kapena kulengeza zochita zake zonse zotamandika?+

 3 Osangalala ndi anthu amene amachita zinthu mwachilungamo,

Amene amachita zinthu zolungama nthawi zonse.+

 4 Ndikumbukireni inu Yehova, pamene mukusonyeza anthu anu kukoma mtima.+

Ndisamalireni ndi kundipulumutsa,

 5 Kuti ndisangalale ndi ubwino umene mumasonyeza osankhidwa anu,+

Kuti ndikondwere limodzi ndi mtundu wanu,

Ndiponso kuti ndikutamandeni monyadira pamodzi ndi cholowa chanu.

 6 Tachimwa mofanana ndi makolo athu.+

Tachita zinthu zolakwika, tachita zinthu zoipa.+

 7 Makolo athu ku Iguputo, sanayamikire* ntchito zanu zodabwitsa.

Sanakumbukire chikondi chanu chokhulupirika chomwe ndi chochuluka,

Koma anapanduka panyanja, pafupi ndi Nyanja Yofiira.+

 8 Koma Mulungu anawapulumutsa kuti dzina lake lilemekezedwe,+

Kuti mphamvu zake zidziwike.+

 9 Iye analamula* ndipo Nyanja Yofiira inauma.

Anatsogolera anthu ake kudutsa pakati pa madzi akuya ngati akudutsa mʼchipululu.+

10 Anawapulumutsa mʼmanja mwa anthu amene ankadana nawo+

Ndipo anawawombola mʼmanja mwa mdani.+

11 Madzi anamiza adani awo,

Moti panalibe ngakhale mmodzi amene anapulumuka.*+

12 Zitatero anakhulupirira zimene anawalonjeza.+

Anayamba kumuimbira nyimbo zomutamanda.+

13 Koma mofulumira anaiwala zimene Mulungu anachita.+

Sanadikire kuti Mulungu awapatse malangizo.

14 Iwo anasonyeza mtima wadyera mʼchipululu,+

Ndipo anayesa Mulungu mʼchipululumo.+

15 Mulungu anawapatsa zimene anapempha,

Koma anawagwetsera matenda amene anawachititsa kuti awonde kwambiri.+

16 Mumsasa, iwo anayamba kuchitira nsanje Mose

Ndiponso Aroni,+ woyera wa Yehova.+

17 Kenako dziko lapansi linatseguka ndipo linameza Datani,

Nʼkukwirira anthu onse amene anali kumbali ya Abiramu.+

18 Moto unayaka pakati pa gulu lawo.

Malawi amoto anapsereza oipa.+

19 Iwo anapanga mwana wa ngʼombe ku Horebe,

Ndipo anagwadira fano lachitsulo.*+

20 Anasinthanitsa ulemerero wanga

Ndi chifaniziro cha ngʼombe yamphongo yodya udzu.+

21 Iwo anaiwala Mulungu,+ Mpulumutsi wawo,

Amene anachita zinthu zazikulu ku Iguputo,+

22 Amene anachita zodabwitsa mʼdziko la Hamu,+

Amene anachita zochititsa mantha pa Nyanja Yofiira.+

23 Iye anangotsala pangʼono kulamula kuti awonongedwe,

Koma Mose wosankhidwa wake, anamuchonderera*

Kuti asawagwetsere mkwiyo wake wowononga.+

24 Pa nthawiyo iwo ananyoza dziko losiririka,+

Ndipo analibe chikhulupiriro pa zimene anawalonjeza.+

25 Anapitiriza kungʼungʼudza mʼmatenti awo.+

Iwo sanamvere mawu a Yehova.+

26 Choncho Mulungu anawalumbirira atakweza dzanja lake,

Kuti adzachititsa kuti afere mʼchipululu.+

27 Adzachititsa kuti mbadwa zawo ziphedwe ndi anthu a mitundu ina,

Ndiponso kuwamwaza mʼmayiko osiyanasiyana.+

28 Kenako iwo anayamba kulambira* Baala wa ku Peori,+

Ndipo anadya nsembe zoperekedwa kwa akufa.*

29 Iwo anamukwiyitsa chifukwa cha zochita zawo,+

Ndipo pakati pawo panagwa mliri.+

30 Koma Pinihasi ataimirira nʼkuchitapo kanthu,

Mliriwo unatha.+

31 Ndipo Pinihasi ankaonedwa kuti ndi wolungama

Ku mibadwo yonse mpaka kalekale.+

32 Iwo anamukwiyitsanso pa madzi a ku Meriba,*

Moti Mose sizinamuyendere bwino chifukwa cha anthu amenewa.+

33 Iwo anamukwiyitsa

Ndipo Mose analankhula mosaganiza bwino.+

34 Iwowa sanawononge mitundu ina ya anthu,+

Ngati mmene Yehova anawalamulira.+

35 Koma anayamba kusakanikirana ndi anthu a mitundu ina,+

Nʼkuyamba* kuchita zinthu ngati mmene iwo ankachitira.+

36 Ankatumikira mafano awo,+

Ndipo mafanowo anakhala msampha kwa iwo.+

37 Ankapereka nsembe ana awo aamuna

Komanso ana awo aakazi kwa ziwanda.+

38 Ankakhetsa magazi a anthu osalakwa,+

Magazi a ana awo aamuna komanso a ana awo aakazi,

Amene anawapereka nsembe kwa mafano a ku Kanani.+

Ndipo dzikolo linaipa ndi magazi amene iwo anakhetsa.

39 Iwo anakhala odetsedwa chifukwa cha ntchito zawo.

Anachita uhule ndi milungu ina chifukwa cha zochita zawo.+

40 Choncho mkwiyo wa Yehova unayakira anthu ake,

Ndipo iye anayamba kunyansidwa ndi cholowa chake.

41 Mobwerezabwereza ankawapereka mʼmanja mwa anthu a mitundu ina,+

Kuti anthu amene ankadana nawo aziwalamulira.+

42 Adani awo ankawapondereza,

Ndipo anali pansi pa ulamuliro wawo.

43 Nthawi zambiri ankawapulumutsa,+

Koma iwo ankamupandukira komanso sankamvera,+

Ndipo ankawonongedwa chifukwa cha zolakwa zawo.+

44 Koma Mulungu ankaona mavuto amene akukumana nawo+

Ndipo ankamva kulira kwawo kopempha thandizo.+

45 Pofuna kuwathandiza iye ankakumbukira pangano lake,

Ndipo ankawamvera chisoni* chifukwa cha chikondi chake chokhulupirika chomwe ndi chachikulu.*+

46 Iye ankachititsa kuti anthu onse amene anawagwira ukapolo+

Awamvere chisoni.

47 Tipulumutseni inu Yehova Mulungu wathu,+

Ndi kutisonkhanitsa pamodzi kuchokera mʼmitundu ina,+

Kuti titamande dzina lanu loyera,

Komanso kuti tikutamandeni mosangalala.+

48 Atamandike Yehova, Mulungu wa Isiraeli,

Mpaka kalekale.*+

Ndipo anthu onse anene kuti, “Ame!”

Tamandani Ya,*

BUKU LA 5

(Masalimo 107-150)

107 Yamikani Yehova, chifukwa iye ndi wabwino.+

Chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapobe mpaka kalekale.+

 2 Anthu amene Yehova anawawombola anene zimenezi,

Anthu amene anawawombola mʼmanja mwa mdani,*+

 3 Anthu amene anawasonkhanitsa pamodzi kuchokera mʼmayiko osiyanasiyana,+

Kuchokera kumʼmawa komanso kumadzulo,*

Kuchokera kumpoto komanso kumʼmwera.+

 4 Iwo ankayendayenda mʼchipululu mopanda kanthu.

Sanapeze njira yopita kumzinda woti azikhalamo.

 5 Anali ndi njala komanso ludzu.

Anafooka kwambiri chifukwa chotopa.

 6 Iwo anapitiriza kufuulira Yehova mʼmasautso awo,+

Ndipo anawalanditsa ku mavuto awo.+

 7 Anawayendetsa mʼnjira yabwino,+

Kuti akafike kumzinda woti azikhalamo.+

 8 Anthu ayamike Yehova+ chifukwa cha chikondi chake chokhulupirika,

Ndiponso chifukwa cha ntchito zake zodabwitsa zimene wachitira ana a anthu.+

 9 Chifukwa iye wathetsa ludzu la anthu aludzu

Ndipo anthu anjala wawadyetsa zinthu zabwino.+

10 Ena ankakhala mumdima wandiweyani,

Anali akaidi amene ankavutika atamangidwa maunyolo.

11 Chifukwa anapandukira mawu a Mulungu,

Ananyoza malangizo a Wamʼmwambamwamba.+

12 Choncho Mulungu anawagwetsera mavuto kuti akhale ndi mtima wodzichepetsa.+

Iwo anapunthwa ndipo panalibe wowathandiza.

13 Iwo anaitana Yehova kuti awathandize mʼmasautso awo,

Ndipo iye anawapulumutsa ku mavuto awo.

14 Iye anawatulutsa mumdima wandiweyani,

Ndipo anadula maunyolo amene anamangidwa nawo.+

15 Anthu ayamike Yehova chifukwa cha chikondi chake chokhulupirika,+

Ndiponso chifukwa cha ntchito zake zodabwitsa zimene wachitira ana a anthu.

16 Chifukwa iye wathyola zitseko zakopa,*

Komanso wadula mipiringidzo yachitsulo.+

17 Anali opusa ndipo anakumana ndi mavuto+

Chifukwa cha zolakwa zawo komanso machimo awo.+

18 Analibe chilakolako* cha chakudya chilichonse,

Iwo anayandikira khomo la imfa.

19 Iwo ankaitana Yehova kuti awathandize mʼmasautso awo.

Ndipo iye ankawapulumutsa ku mavuto awo.

20 Iye ankalamula kuti achire ndipo ankachiradi+

Komanso ankawapulumutsa kuti asafe.

21 Anthu ayamike Yehova chifukwa cha chikondi chake chokhulupirika,

Ndiponso chifukwa cha ntchito zake zodabwitsa zimene wachitira ana a anthu.

22 Iwo apereke nsembe zoyamikira,+

Komanso alengeze ntchito zake pofuula mosangalala.

23 Anthu amene amayenda panyanja mʼsitima,

Amene amachita malonda pamadzi ambiri,+

24 Iwo aona ntchito za Yehova,

Ndiponso ntchito zake zodabwitsa mʼmadzi akuya.+

25 Aona mmene mawu ake amayambitsira mphepo yamkuntho,+

Nʼkuchititsa mafunde panyanja.

26 Mafundewo amakweza anthuwo mʼmwamba

Kenako amawatsitsa pansi pakati pa nyanja.

Kulimba mtima kwawo kumatha chifukwa cha tsoka limene akuliyembekezera.

27 Amayenda peyupeyu ndipo amadzandira ngati munthu woledzera,

Ndipo luso lawo lonse limakhala lopanda ntchito.+

28 Kenako amafuulira Yehova mʼmasautso awo,+

Ndipo iye amawapulumutsa mʼmavuto awo.

29 Iye amachititsa kuti mphepo yamkuntho ikhale bata,

Mafunde apanyanja amadekha.+

30 Iwo amasangalala mafundewo akatha,

Ndipo Mulungu amawatsogolera kudoko limene iwo akufuna.

31 Anthu ayamike Yehova chifukwa cha chikondi chake chokhulupirika,

Ndiponso chifukwa cha ntchito zake zodabwitsa zimene wachitira ana a anthu.+

32 Amukweze mumpingo wa anthu,+

Ndipo amutamande pamsonkhano* wa anthu achikulire.

33 Amasandutsa mitsinje kukhala chipululu,

Ndiponso akasupe a madzi kukhala malo ouma.+

34 Nthaka yobala zipatso amaisandutsa dziko lopanda chonde,+

Chifukwa cha kuipa kwa anthu okhala mmenemo.

35 Chipululu amachisandutsa dambo la madzi,

Ndipo dziko louma amalisandutsa dera la akasupe amadzi.+

36 Amachititsa kuti anthu anjala azikhala kumeneko,+

Kuti amangeko mzinda woti azikhalamo.+

37 Anthuwo amafesa mbewu nʼkulima minda ya mpesa,+

Kuti akhale ndi zokolola.+

38 Mulungu amawadalitsa ndipo amachuluka kwambiri.

Iye salola kuti ngʼombe zawo zichepe.+

39 Koma iwo anakhala ochepa ndipo anachititsidwa manyazi

Chifukwa choponderezedwa, masoka komanso chisoni.

40 Mulungu amachititsa manyazi anthu olemekezeka

Ndipo amawachititsa kuti azingoyendayenda mʼchipululu mmene mulibe njira.+

41 Koma amateteza* anthu osauka kuti asaponderezedwe+

Ndipo amachulukitsa mabanja awo ngati gulu la nkhosa.

42 Olungama amaona zimenezi ndipo amasangalala.+

Koma anthu onse osalungama amatseka pakamwa.+

43 Aliyense wanzeru aona zinthu zimenezi+

Ndipo aganizira mofatsa zimene Yehova wachita posonyeza chikondi chake chokhulupirika.+

Nyimbo ndi Salimo la Davide.

108 Ndatsimikiza mtima, Inu Mulungu,

Ndidzakuimbirani nyimbo ndi moyo wanga wonse* pogwiritsa ntchito zipangizo zoimbira.+

 2 Dzuka, iwe choimbira cha zingwe, ndi iwenso zeze.+

Ine ndidzadzuka mʼbandakucha.

 3 Ndidzakutamandani pakati pa mitundu ya anthu, inu Yehova.

Ndidzaimba nyimbo zokutamandani pakati pa mitundu ya anthu.

 4 Chifukwa chikondi chanu chokhulupirika nʼchachikulu moti chafika kumwamba,+

Ndipo kukhulupirika kwanu kwafika kuthambo.

 5 Inu Mulungu, kwezekani kupitirira kumwamba.

Ulemerero wanu ukhale padziko lonse lapansi.+

 6 Kuti anthu amene mumawakonda apulumutsidwe,

Tipulumutseni ndi dzanja lanu lamanja ndipo mundiyankhe.+

 7 Popeza ndi woyera,* Mulungu walankhula kuti:

“Ndidzasangalala popereka Sekemu+ ngati cholowa,

Ndipo ndidzayezera anthu anga malo mʼchigwa cha Sukoti.+

 8 Giliyadi+ ndi wanga, ngati mmene zilili ndi Manase,

Ndipo Efuraimu ndi chipewa* choteteza mutu wanga.+

Yuda akuimira mphamvu zanga zolamula.+

 9 Mowabu ndi beseni langa losambiramo.+

Edomu ndidzamuponyera nsapato zanga.+

Ndidzafuula mosangalala chifukwa chogonjetsa Filisitiya.”+

10 Ndi ndani amene adzandibweretse kumzinda wokhala ndi mpanda wolimba kwambiri?

Ndi ndani amene adzanditsogolere mpaka kukafika ku Edomu?+

11 Kodi si inu Mulungu amene munatikana,

Mulungu wathu, amene simukutsogoleranso magulu athu ankhondo?+

12 Tithandizeni pamene tikukumana ndi mavuto,+

Chifukwa chipulumutso chochokera kwa munthu nʼchopanda pake.+

13 Mulungu adzatipatsa mphamvu,+

Ndipo adzapondaponda adani athu.+

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ndi Salimo la Davide.

109 Inu Mulungu amene ndimakutamandani,+ musakhale chete.

 2 Chifukwa anthu oipa ndiponso achinyengo akundinenera zinthu zoipa

Iwo akulankhula zinthu zabodza zokhudza ine.+

 3 Andizungulira ndipo akulankhula mawu osonyeza kuti amadana nane,

Komanso akundiukira popanda chifukwa.+

 4 Ndikawasonyeza chikondi amandiimba mlandu,+

Koma ine ndimapitiriza kupemphera.

 5 Ndikawachitira zabwino iwo amandibwezera zoipa+

Ndikawasonyeza chikondi amadana nane.+

 6 Muikireni woweruza woipa,

Ndipo kudzanja lake lamanja kuime amene akumuimba mlandu.*

 7 Akamaweruzidwa apezeke kuti ndi wolakwa.*

Ndipo ngakhale pemphero lake lizionedwa ngati tchimo.+

 8 Masiku a moyo wake akhale ochepa.+

Udindo wake monga woyangʼanira utengedwe ndi munthu wina.+

 9 Ana ake* akhale amasiye,

Ndipo mkazi wake akhalenso wamasiye.

10 Ana ake* aziyendayenda ndipo akhale opemphapempha.

Azichoka mʼmabwinja mmene akukhala, nʼkukafunafuna chakudya.

11 Wangongole alande* zonse zimene ali nazo,

Ndipo anthu achilendo alande zinthu zake.

12 Pasapezeke womuchitira chifundo,*

Ndipo pasapezeke aliyense wosonyeza kukoma mtima kwa ana ake amasiyewo.

13 Mbadwa zake ziphedwe.+

Dzina lawo lisadzakumbukiridwe mu mʼbadwo wotsatira.

14 Yehova akumbukire zolakwa za makolo ake,+

Ndipo tchimo la mayi ake lisafufutidwe.

15 Nthawi zonse Yehova azikumbukira zimene achita.

Ndipo achititse kuti asadzakumbukiridwenso padziko lapansi.+

16 Chifukwa chakuti sanakumbukire kusonyeza chifundo,*+

Koma anapitiriza kuthamangitsa munthu woponderezedwa,+ wosauka komanso wosweka mtima,

Kuti amuphe.+

17 Iye ankakonda kutemberera, choncho matemberero anabwera pa iye.

Analibe mtima wofuna kudalitsa, choncho sanalandire madalitso.

18 Iye anavekedwa matemberero ngati chovala.

Ndipo anathiridwa mʼthupi mwake ngati madzi,

Ndiponso mʼmafupa ake ngati mafuta.

19 Matemberero ake akhale ngati nsalu imene amadziphimba nayo,+

Komanso ngati lamba amene amavala nthawi zonse.

20 Amenewa ndi malipiro amene Yehova amapereka kwa amene amalimbana nane+

Komanso kwa amene amalankhula zinthu zoipa zokhudza ine.

21 Koma inu, Yehova Ambuye Wamkulu Koposa,

Ndithandizeni kuti dzina lanu lilemekezedwe.+

Ndipulumutseni chifukwa chikondi chanu chokhulupirika nʼchabwino.+

22 Chifukwa ndavutika ndipo ndasauka,+

Ndipo mtima wanga wabaidwa mkati mwanga.+

23 Ine ndikutha ngati chithunzithunzi chimene chimazimiririka.

Ndili ngati dzombe lomwe lakutumulidwa pa chovala.

24 Mawondo anga akunjenjemera chifukwa chosala kudya,

Ndawonda ndipo ndatsala mafupa okhaokha.*

25 Iwo akumandinyoza.+

Akandiona akumapukusa mitu yawo.+

26 Ndithandizeni, inu Yehova Mulungu wanga.

Ndipulumutseni ndi chikondi chanu chokhulupirika.

27 Iwo adziwe kuti zimenezi zachitika chifukwa cha dzanja lanu.

Adziwe kuti inu Yehova mwachita zimenezi.

28 Alekeni anditemberere, koma inu mundipatse madalitso.

Iwo akaimirira kuti andiukire, inu muwachititse manyazi,

Koma lolani ine mtumiki wanu kuti ndisangalale.

29 Amene akulimbana ndi ine avekedwe manyazi.

Avale manyaziwo ngati kuti avala mkanjo.*+

30 Pakamwa panga padzatamanda Yehova ndi mtima wonse.

Ndidzamutamanda pamaso pa anthu ambiri.+

31 Chifukwa adzaima kudzanja lamanja la munthu wosauka,

Kuti amupulumutse kwa amene akumuweruza mopanda chilungamo.

Salimo ndi Nyimbo ya Davide.

110 Yehova anauza Ambuye wanga kuti:

“Khala kudzanja langa lamanja+

Mpaka nditaika adani ako kuti akhale chopondapo mapazi ako.”+

 2 Yehova adzatambasula ndodo yako yachifumu kuti ulamulirenso madera ena osati mu Ziyoni mokha. Iye adzanena kuti:

“Pita pakati pa adani ako ndipo ukawagonjetse.”+

 3 Anthu ako adzadzipereka mofunitsitsa pa tsiku limene udzatsogolera asilikali ako kunkhondo.*

Gulu la achinyamata amene ali ngati mame amʼbandakucha likukuthandiza.

Iwo ndi apadera kwa ine komanso ndi okongola.

 4 Yehova walumbira ndipo sadzasintha maganizo. Iye wati:

“Iwe ndiwe wansembe mpaka kalekale,+

Mofanana ndi unsembe wa Melekizedeki!”+

 5 Yehova adzakhala kudzanja lako lamanja.+

Iye adzaphwanya mafumu pa tsiku la mkwiyo wake.+

 6 Adzapereka chiweruzo ku* mitundu ya anthu.+

Adzachititsa kuti mʼdziko mudzaze mitembo ya anthu.+

Adzaphwanya mtsogoleri* wa dziko lalikulu.*

 7 Ali mʼnjira, iye* adzamwa madzi amumtsinje.

Choncho adzatukula kwambiri mutu wake.

111 Tamandani Ya!*+

א [Aleph]

Ndidzatamanda Yehova ndi mtima wanga wonse+

ב [Beth]

Pamsonkhano wa anthu owongoka mtima komanso mumpingo.

ג [Gimel]

 2 Ntchito za Yehova ndi zazikulu,+

ד [Daleth]

Anthu onse amene amasangalala nazo amaziphunzira.+

ה [He]

 3 Zochita zake zimasonyeza ulemerero ndi ulemu,

ו [Waw]

Ndipo chilungamo chake chidzakhalapobe kwamuyaya.+

ז [Zayin]

 4 Iye amachititsa kuti ntchito zake zodabwitsa zizikumbukiridwa.+

ח [Heth]

Yehova ndi wokoma mtima* ndiponso wachifundo.+

ט [Teth]

 5 Iye amapereka chakudya kwa anthu amene amamuopa.+

י [Yod]

Amakumbukira pangano lake mpaka kalekale.+

כ [Kaph]

 6 Waululira anthu ake ntchito zake zamphamvu

ל [Lamed]

Powapatsa cholowa cha anthu a mitundu ina.+

מ [Mem]

 7 Ntchito za manja ake zimadziwika ndi choonadi ndiponso chilungamo.+

נ [Nun]

Malamulo onse amene amapereka ndi odalirika.+

ס [Samekh]

 8 Ndi odalirika* nthawi zonse, kuyambira panopa mpaka kalekale.

ע [Ayin]

Maziko ake ndi choonadi komanso chilungamo.+

פ [Pe]

 9 Wawombola anthu ake.+

צ [Tsade]

Walamula kuti pangano lake likhalepo mpaka kalekale.

ק [Qoph]

Dzina lake ndi loyera komanso lochititsa mantha.+

ר [Resh]

10 Chiyambi cha nzeru ndi kuopa Yehova.+

ש [Sin]

Onse otsatira malamulo ake amasonyeza kuti ndi ozindikira.+

ת [Taw]

Iye ayenera kutamandidwa mpaka kalekale.

112 Tamandani Ya!*+

א [Aleph]

Wosangalala ndi munthu amene amaopa Yehova,+

ב [Beth]

Amene amasangalala kwambiri ndi malamulo ake.+

ג [Gimel]

 2 Mbadwa zake zidzakhala zamphamvu padziko lapansi,

ד [Daleth]

Ndipo mʼbadwo wa anthu olungama udzadalitsidwa.+

ה [He]

 3 Zinthu zamtengo wapatali ndiponso chuma zili mʼnyumba yake,

ו [Waw]

Ndipo chilungamo chake chidzakhalapo kwamuyaya.

ז [Zayin]

 4 Kwa anthu owongoka mtima iye amawala ngati kuwala kumene kumaunika mumdima.+

ח [Heth]

Iye ndi wokoma mtima,* wachifundo+ komanso wolungama.

ט [Teth]

 5 Munthu amene amakongoza ena mosaumira, zinthu zimamuyendera bwino.+

י [Yod]

Iye amachita zinthu mwachilungamo.

כ [Kaph]

 6 Sadzagwedezeka ngakhale pangʼono.+

ל [Lamed]

Wolungama adzakumbukiridwa mpaka kalekale.+

מ [Mem]

 7 Sadzaopa uthenga woipa.+

נ [Nun]

Mtima wake ndi wokhazikika ndipo amadalira Yehova.+

ס [Samekh]

 8 Mtima wake sukugwedezeka* ndipo sakuchita mantha,+

ע [Ayin]

Pamapeto pake adzayangʼana adani ake, adaniwo atagonjetsedwa.+

פ [Pe]

 9 Iye wagawira ena mowolowa manja, wapereka kwa anthu osauka.+

צ [Tsade]

Chilungamo chake chidzakhalapo mpaka kalekale.+

ק [Qoph]

Mphamvu zake zidzawonjezeka* chifukwa cha ulemerero.

ר [Resh]

10 Woipa adzaona zimenezi ndipo adzakhumudwa.

ש [Shin]

Adzakukuta mano ndi kusungunuka.

ת [Taw]

Zimene anthu oipa amalakalaka sizidzachitika.+

113 Tamandani Ya!*

Inu atumiki a Yehova, mutamandeni,

Tamandani dzina la Yehova.

 2 Dzina la Yehova litamandike

Kuyambira panopa mpaka kalekale.+

 3 Kuyambira kotulukira dzuwa mpaka kumene limalowera,

Dzina la Yehova litamandidwe.+

 4 Yehova ali pamwamba pa mitundu yonse ya anthu.+

Ulemerero wake uli pamwamba pa kumwamba.+

 5 Ndi ndani angafanane ndi Yehova Mulungu wathu,+

Amene amakhala* pamwamba?

 6 Iye amatsika mʼmunsi kuti aone kumwamba ndi dziko lapansi.+

 7 Amadzutsa munthu wonyozeka kumuchotsa mʼfumbi.

Amanyamula munthu wosauka kumuchotsa pamulu wa phulusa*+

 8 Kuti amukhazike pamodzi ndi anthu olemekezeka,

Pamodzi ndi anthu olemekezeka pakati pa anthu a Mulungu.

 9 Amachititsa mkazi wosabereka kukhala ndi ana

Kukhala mayi wosangalala wa ana.*+

Tamandani Ya!*

114 Isiraeli atatuluka mu Iguputo,+

Nyumba ya Yakobo itatuluka pakati pa anthu olankhula chilankhulo chachilendo,

 2 Yuda anakhala malo ake opatulika,

Ndipo Isiraeli linakhala dziko limene ankalilamulira.+

 3 Nyanja inaona zimenezi ndipo inathawa,+

Yorodano anabwerera mʼmbuyo.+

 4 Mapiri anadumphadumpha ngati nkhosa zamphongo,+

Zitunda zinadumphadumpha ngati ana a nkhosa.

 5 Nʼchiyani chinakupangitsa kuti uthawe, nyanja iwe?+

Nʼchifukwa chiyani iwe Yorodano unabwerera mʼmbuyo?+

 6 Nanga inu mapiri, nʼchifukwa chiyani munkadumphadumpha ngati nkhosa zamphongo?

Inunso zitunda, nʼchifukwa chiyani munkadumphadumpha ngati ana a nkhosa?

 7 Iwe dziko lapansi, njenjemera chifukwa cha Ambuye,

Chifukwa cha Mulungu wa Yakobo,+

 8 Amene amasintha thanthwe kukhala dambo la madzi,

Komanso mwala wa nsangalabwi kukhala akasupe a madzi.+

115 Ife sitikuyenera, inu Yehova, ife sitikuyenera,

Koma ulemerero ukuyenera kupita ku dzina lanu+

Chifukwa cha kukhulupirika kwanu komanso chikondi chanu chokhulupirika.+

 2 Musalole kuti anthu a mitundu ina azinena kuti:

“Mulungu wawo ali kuti?”+

 3 Mulungu wathu ali kumwamba.

Iye amachita chilichonse chimene chamusangalatsa.

 4 Mafano awo ndi opangidwa ndi siliva komanso golide,

Ntchito ya manja a anthu.+

 5 Pakamwa ali napo koma sangalankhule.+

Maso ali nawo koma sangaone.

 6 Makutu ali nawo koma sangamve.

Mphuno ali nayo koma sanganunkhize.

 7 Manja ali nawo koma sakhudza kanthu.

Mapazi ali nawo koma sangayende.+

Satulutsa mawu ndi mmero wawo.+

 8 Anthu amene amawapanga adzafanana nawo,+

Chimodzimodzinso anthu onse amene amakhulupirira mafanowo.+

 9 Aisiraeli inu, khulupirirani Yehova,+

Iye ndi amene amakuthandizani komanso ndi chishango chanu.+

10 Inu nyumba ya Aroni,+ khulupirirani Yehova,

Iye ndi amene amakuthandizani komanso ndi chishango chanu.

11 Inu amene mumaopa Yehova, khulupirirani Yehova,+

Iye ndi amene amakuthandizani komanso ndi chishango chanu.+

12 Yehova akutikumbukira ndipo adzatidalitsa.

Adzadalitsa nyumba ya Isiraeli.+

Adzadalitsa nyumba ya Aroni.

13 Yehova adzadalitsa anthu onse amene amamuopa,

Aangʼono ndi aakulu omwe.

14 Yehova adzakuchulukitsani,

Inuyo komanso ana anu.*+

15 Yehova akudalitseni,+

Amene anapanga kumwamba ndi dziko lapansi.+

16 Kunena za kumwamba, kumwamba ndi kwa Yehova,+

Koma dziko lapansi analipereka kwa ana a anthu.+

17 Akufa satamanda Ya,+

Ngakhalenso aliyense amene amatsikira kulichete.+

18 Koma ife tidzatamanda Ya

Kuyambira panopa mpaka kalekale.

Tamandani Ya!*

116 Ndimakonda Yehova

Chifukwa amamva mawu anga komanso kuchonderera kwanga kopempha thandizo.+

 2 Amatchera khutu lake nʼkundimvetsera,*+

Ndipo ndidzaitanira pa iye moyo wanga wonse.*

 3 Zingwe za imfa zinandikulunga.

Ndinkangomva ngati ndatsala pangʼono kufa.+

Ndinavutika chifukwa cha nkhawa komanso chisoni.+

 4 Koma ndinaitana pa dzina la Yehova kuti:+

“Inu Yehova, ndipulumutseni!”

 5 Yehova ndi wokoma mtima* komanso wolungama.+

Mulungu wathu ndi wachifundo.+

 6 Yehova amateteza anthu osadziwa zambiri.+

Ndinafooka chifukwa cha nkhawa koma iye anandipulumutsa.

 7 Moyo wanga upumulenso,

Chifukwa Yehova wandichitira zinthu mokoma mtima.

 8 Inu mwandipulumutsa ku imfa,

Mwapukuta misozi yanga ndipo mwateteza phazi langa kuti lisapunthwe.+

 9 Ndidzayenda pamaso pa Yehova mʼdziko la anthu amoyo.

10 Ndinali ndi chikhulupiriro, nʼchifukwa chake ndinalankhula.+

Ndinavutika kwambiri.

11 Nditapanikizika ndinati:

“Munthu aliyense ndi wabodza.”+

12 Yehova ndidzamubwezera chiyani

Pa zabwino zonse zimene wandichitira?

13 Ndidzamwa zamʼkapu yachipulumutso,*

Ndipo ndidzaitana pa dzina la Yehova.

14 Ndidzakwaniritsa malonjezo anga kwa Yehova,

Pamaso pa anthu ake onse.+

15 Mʼmaso mwa Yehova

Imfa ya anthu ake okhulupirika ndi yopweteka kwambiri.*+

16 Ndikukupemphani, inu Yehova,

Chifukwa ine ndi mtumiki wanu.

Ndine mtumiki wanu, mwana wa kapolo wanu wamkazi.

Mwamasula zingwe zimene anandimanga nazo.+

17 Ndidzapereka nsembe zoyamikira kwa inu,+

Ndipo ndidzaitana pa dzina la Yehova.

18 Ndidzakwaniritsa malonjezo anga kwa Yehova,+

Pamaso pa anthu ake onse,+

19 Mʼmabwalo a nyumba ya Yehova,+

Pakati pa iwe Yerusalemu.

Tamandani Ya!*+

117 Tamandani Yehova, inu mitundu yonse ya anthu.+

Mulemekezeni, inu anthu a mitundu yonse.*+

 2 Chifukwa chikondi chokhulupirika chimene amatisonyeza ndi chachikulu.+

Kukhulupirika+ kwa Yehova kudzakhalapo mpaka kalekale.+

Tamandani Ya!*+

118 Yamikani Yehova, chifukwa iye ndi wabwino.+

Chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale.

 2 Isiraeli anene kuti:

“Chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale.”

 3 Anthu amʼnyumba ya Aroni tsopano anene kuti:

“Chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale.”

 4 Anthu amene amaopa Yehova tsopano anene kuti:

“Chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale.”

 5 Nditavutika ndinaitana Ya.*

Ya anandiyankha nʼkundipititsa pamalo otetezeka.*+

 6 Yehova ali kumbali yanga, sindidzaopa.+

Munthu angandichite chiyani?+

 7 Yehova ali kumbali yanga ndipo akundithandiza.+

Ndidzayangʼana anthu amene amadana nane atagonja.+

 8 Kuthawira kwa Yehova nʼkwabwino

Kusiyana ndi kudalira anthu.+

 9 Kuthawira kwa Yehova nʼkwabwino

Kusiyana ndi kudalira akalonga.+

10 Mitundu yonse ya anthu inandizungulira,

Koma mʼdzina la Yehova,

Ndinaithamangitsira kutali.+

11 Mitunduyo inandizungulira, ndithu inandizungulira kumbali zonse.

Koma mʼdzina la Yehova

Ndinaithamangitsira kutali.

12 Inandizungulira ngati njuchi,

Koma inathimitsidwa mwamsanga ngati moto umene uli pakati pa minga.

Mʼdzina la Yehova,

Ndinaithamangitsira kutali.+

13 Ndinakankhidwa kwambiri kuti ndigwe,

Koma Yehova anandithandiza.

14 Ya ndi malo anga obisalapo komanso mphamvu yanga,

Iye wakhala chipulumutso changa.+

15 Phokoso lachisangalalo komanso chipulumutso*

Likumveka mʼmatenti a anthu olungama.

Dzanja lamanja la Yehova likusonyeza mphamvu zake.+

16 Dzanja lamanja la Yehova lakwera mʼmwamba chifukwa wapambana.

Dzanja lamanja la Yehova likusonyeza mphamvu zake.+

17 Sindidzafa, koma ndidzakhala ndi moyo,

Kuti ndilengeze ntchito za Ya.+

18 Ya anandilanga mwamphamvu,+

Koma sanalole kuti ndife.+

19 Nditsegulireni mageti achilungamo.+

Ndidzalowa mmenemo ndipo ndidzatamanda Ya.

20 Ili ndi geti la Yehova.

Olungama adzalowa pamenepo.+

21 Ndidzakutamandani, chifukwa munandiyankha+

Ndipo munakhala chipulumutso changa.

22 Mwala umene omanga nyumba anaukana

Wakhala mwala wapakona* wofunika kwambiri.+

23 Umenewu wachokera kwa Yehova,+

Ndipo ndi wodabwitsa mʼmaso mwathu.+

24 Ili ndi tsiku limene Yehova wapanga.

Tidzakondwera ndi kusangalala pa tsiku limeneli.

25 Yehova tikukupemphani, chonde tipulumutseni.

Yehova, chonde tithandizeni kuti tipambane.

26 Wodalitsidwa ndi amene akubwera mʼdzina la Yehova.+

Tikupempha kuti Yehova akudalitseni mʼnyumba yake.

27 Yehova ndi Mulungu.

Iye amatipatsa kuwala.+

Tiyeni tikhale limodzi ndi gulu la anthu amene akupita kuchikondwerero atanyamula nthambi mʼmanja mwawo,+

Mpaka kukafika panyanga za guwa lansembe.+

28 Inu ndinu Mulungu wanga ndipo ndidzakutamandani.

Ndinu Mulungu wanga ndipo ndidzakukwezani.+

29 Yamikani Yehova,+ chifukwa iye ndi wabwino.

Chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale.+

א [Aleph]

119 Osangalala ndi anthu amene salakwitsa kanthu* mʼnjira zawo,

Amene amatsatira chilamulo cha Yehova.+

 2 Osangalala ndi anthu amene amasunga zikumbutso zake,+

Amene amamufunafuna ndi mtima wawo wonse.+

 3 Iwo sachita zinthu zosalungama.

Amayenda mʼnjira zake.+

 4 Inu mwalamula

Kuti tizitsatira malamulo anu mosamala.+

 5 Zikanakhala bwino ndikanakhala wolimba*+

Kuti nditsatire malangizo anu.

 6 Zikanatero sindikanachita manyazi,+

Pa nthawi imene ndikuganizira malamulo anu onse.

 7 Ndidzakutamandani ndi mtima wowongoka,

Pamene ndikuphunzira zigamulo zanu zolungama.

 8 Ndidzasunga malangizo anu.

Choncho musandisiye ndekha.

ב [Beth]

 9 Kodi wachinyamata angakhale bwanji woyera pa moyo wake?

Akamadzifufuza nthawi zonse kuti aone ngati zochita zake zikugwirizana ndi mawu anu.+

10 Ndimakufunafunani ndi mtima wanga wonse.

Musalole kuti ndisochere nʼkuchoka pa malamulo anu.+

11 Ndasunga mosamala mawu anu mumtima mwanga+

Kuti ndisakuchimwireni.+

12 Mutamandike, inu Yehova.

Ndiphunzitseni malamulo anu.

13 Ndi milomo yanga ndalengeza

Zigamulo zonse zimene inu mwanena.

14 Ndimasangalala ndi zikumbutso zanu,+

Kuposa mmene ndimasangalalira ndi zinthu zina zonse zamtengo wapatali.+

15 Ndidzaganizira mozama* malamulo anu,+

Ndipo ndidzayangʼanitsitsa njira zanu.+

16 Ndimakonda malamulo anu.

Sindidzaiwala mawu anu.+

ג [Gimel]

17 Ndichitireni zinthu mokoma mtima, ine mtumiki wanu,

Kuti ndikhale ndi moyo komanso kuti ndisunge mawu anu.+

18 Tsegulani maso anga kuti ndione bwinobwino

Zinthu zodabwitsa zamʼchilamulo chanu.

19 Ine ndine mlendo mʼdzikoli.+

Musandibisire malamulo anu.

20 Ndimalakalaka kwambiri

Nditadziwa zigamulo zanu nthawi zonse.

21 Mumadzudzula anthu odzikuza,

Otembereredwa amene akusochera nʼkusiya kutsatira malamulo anu.+

22 Muwachititse kuti asiye* kusandilemekeza komanso kundinyoza,

Chifukwa ndatsatira zikumbutso zanu.

23 Ngakhale pamene akalonga asonkhana pamodzi nʼkumakambirana zoti andiukire,

Ine mtumiki wanu ndimaganizira mozama* malangizo anu.

24 Ndimakonda kwambiri zikumbutso zanu,+

Ndipo zili ngati anthu amene amandipatsa malangizo.+

ד [Daleth]

25 Ndagona pafumbi.+

Ndithandizeni kuti ndikhalebe ndi moyo mogwirizana ndi mawu anu.+

26 Ndinakuuzani za njira zanga ndipo munandiyankha.

Ndiphunzitseni malamulo anu.+

27 Ndithandizeni kumvetsa tanthauzo la* malamulo anu,

Kuti ndiganizire mozama* ntchito zanu zodabwitsa.+

28 Ine ndakhala ndikusowa tulo chifukwa cha chisoni.

Ndilimbitseni mogwirizana ndi mawu anu.

29 Ndithandizeni kuti ndisakhale munthu wachinyengo,+

Ndipo mundikomere mtima pondipatsa chilamulo chanu.

30 Ine ndasankha kuti ndizichita zinthu mokhulupirika.+

Ndimadziwa kuti zigamulo zanu ndi zolungama.

31 Ndimatsatira zikumbutso zanu nthawi zonse.+

Inu Yehova, musalole kuti ndikhumudwe.*+

32 Ndidzatsatira* malamulo anu ndi mtima wonse,

Chifukwa mwandithandiza kuti ndiwamvetse bwino.

ה [He]

33 Ndiphunzitseni inu Yehova,+ kuti ndizichita zinthu mogwirizana ndi malangizo anu,

Ndipo ndidzawatsatira kwa moyo wanga wonse.+

34 Ndithandizeni kuti ndikhale wozindikira

Kuti nditsatire chilamulo chanu,

Ndiponso kuti ndichisunge ndi mtima wanga wonse.

35 Nditsogolereni* mʼnjira ya malamulo anu,+

Chifukwa njira imeneyi imandisangalatsa

36 Ndithandizeni kuti mtima wanga uzikonda zikumbutso zanu,

Osati kupeza phindu mwachinyengo.+

37 Ndithandizeni kuti ndizipewa kuyangʼana zinthu zopanda pake.+

Ndithandizeni kuyenda mʼnjira yanu kuti ndikhalebe ndi moyo.

38 Kwaniritsani zimene munalonjeza* mtumiki wanu,

Kuti anthu azikuopani.

39 Chotsani zinthu zochititsa manyazi zimene ndikuziopa,

Chifukwa zigamulo zanu ndi zabwino.+

40 Taonani mmene ndikulakalakira malamulo anu.

Ndithandizeni kukhalabe ndi moyo mogwirizana ndi chilungamo chanu.

ו [Waw]

41 Ndione chikondi chanu chokhulupirika, inu Yehova,+

Komanso mundipulumutse mogwirizana ndi lonjezo lanu.*+

42 Mukatero ndiyankha amene akundinyoza,

Chifukwa ine ndimadalira mawu anu.

43 Ndithandizeni kuti ndipitirize kunena mawu a choonadi,

Chifukwa ndikuyembekezera* chigamulo chanu.

44 Ndidzasunga chilamulo chanu nthawi zonse,

Mpaka kalekale.+

45 Ndidzayendayenda mʼmalo otetezeka,*+

Chifukwa ndimayesetsa kuphunzira malamulo anu.

46 Ndidzanena zokhudza zikumbutso zanu pamaso pa mafumu,

Ndipo sindidzachita manyazi.+

47 Ndimakonda kwambiri malamulo anu,

Inde, ndimawakonda.+

48 Ndidzapemphera kwa inu nditakweza manja anga chifukwa ndimakonda malamulo anu,+

Ndipo ndidzaganizira mozama* malangizo anu.+

ז [Zayin]

49 Kumbukirani mawu amene* munandiuza ine mtumiki wanu,

Mawu amene mumandipatsa nawo chiyembekezo.*

50 Izi ndi zimene zimandilimbikitsa ndikakhala pamavuto,+

Chifukwa mawu anu andithandiza kuti ndikhalebe ndi moyo.

51 Anthu odzikuza andinyoza koopsa.

Koma ine sindinasiye kutsatira chilamulo chanu.+

52 Ndimakumbukira zigamulo zanu zakalekale+ inu Yehova,

Ndipo zimandilimbikitsa.+

53 Ndakwiya kwambiri chifukwa cha oipa,

Amene akusiya chilamulo chanu.+

54 Kwa ine, malangizo anu ali ngati nyimbo,

Kulikonse kumene ndimakhala.*

55 Usiku ndimakumbukira dzina lanu, inu Yehova,+

Kuti ndisunge chilamulo chanu.

56 Ndakhala ndikuchita zimenezi

Chifukwa ndimatsatira malamulo anu.

ח [Heth]

57 Yehova ndi cholowa changa.+

Ndalonjeza kusunga mawu anu.+

58 Ndikukupemphani* ndi mtima wanga wonse.+

Ndikomereni mtima+ mogwirizana ndi zimene munalonjeza.*

59 Ndaganizira mozama za njira zanga,

Kuti mapazi anga ndiwabwezere ku zikumbutso zanu.+

60 Ndimafulumira ndipo sindizengereza

Kusunga malamulo anu.+

61 Zingwe za oipa zandikulunga,

Koma ine sindinaiwale chilamulo chanu.+

62 Ndimadzuka pakati pa usiku kuti ndikuyamikeni+

Chifukwa cha zigamulo zanu zolungama.

63 Ine ndine mnzawo wa anthu amene amakuopani,

Ndiponso wa anthu amene amasunga malamulo anu.+

64 Inu Yehova, chikondi chanu chokhulupirika chadzaza dziko lapansi.+

Ndiphunzitseni malamulo anu.

ט [Teth]

65 Inu Yehova, mwandichitira zabwino ine mtumiki wanu,

Mogwirizana ndi mawu anu.

66 Ndithandizeni kuti ndikhale wozindikira komanso wodziwa zinthu,+

Chifukwa ndimadalira malamulo anu.

67 Ndisanakumane ndi mavuto ndinkasochera pafupipafupi,*

Koma panopa ndimasunga mawu anu.+

68 Inu ndinu wabwino+ ndipo ntchito zanu ndi zabwino.

Ndiphunzitseni malamulo anu.+

69 Anthu odzikuza akundinenera zinthu zambiri zabodza,

Koma ine ndimasunga malamulo anu ndi mtima wanga wonse.

70 Mitima yawo yauma ngati mwala,*+

Koma ine ndimakonda kwambiri chilamulo chanu.+

71 Zili bwino kuti ndakumana ndi mavuto,+

Kuti ndiphunzire malamulo anu.

72 Chilamulo chimene mwapereka nʼchabwino kwa ine,+

Nʼchabwino kwambiri kuposa ndalama zagolide ndi zasiliva masauzande ambiri.+

י [Yod]

73 Manja anu anandipanga komanso kundiumba.

Ndithandizeni kuti ndikhale wozindikira,

Kuti ndiphunzire malamulo anu.+

74 Amene amakuopani amasangalala akandiona,

Chifukwa mawu anu ndi chiyembekezo changa.*+

75 Inu Yehova, ndikudziwa kuti zigamulo zanu ndi zolungama+

Komanso kuti mwandilanga chifukwa chakuti ndinu wokhulupirika.+

76 Chikondi chanu chokhulupirika+ chindilimbikitse,

Mogwirizana ndi zimene munandilonjeza* ine mtumiki wanu.

77 Ndisonyezeni chifundo kuti ndipitirize kukhala ndi moyo,+

Chifukwa ndimakonda kwambiri chilamulo chanu.+

78 Odzikuza achite manyazi,

Chifukwa amandilakwira popanda chifukwa.

Koma ine ndidzaganizira mozama* malamulo anu.+

79 Anthu amene amakuopani abwerere kwa ine,

Amene amadziwa zikumbutso zanu.

80 Mtima wanga uzitsatira malangizo anu mosalakwitsa kanthu,+

Kuti ndisachite manyazi.+

כ [Kaph]

81 Ine ndikulakalaka chipulumutso chanu,+

Chifukwa mawu anu ndi chiyembekezo changa.*

82 Maso anga akulakalaka mawu anu+

Ndipo ndikunena kuti: “Kodi mudzandilimbikitsa liti?”+

83 Chifukwa ndili ngati thumba lachikopa limene lauma mu utsi,

Koma sindinaiwale malangizo anu.+

84 Kodi ine mtumiki wanu ndidikira mpaka liti?

Kodi anthu amene akundizunza mudzawaweruza liti?+

85 Anthu odzikuza andikumbira dzenje kuti ndigweremo,

Anthu amene safuna kutsatira chilamulo chanu.

86 Malamulo anu onse ndi odalirika.

Anthu akundizunza popanda chifukwa. Chonde, ndithandizeni.+

87 Iwo anangotsala pangʼono kundifafaniza padziko lapansi,

Koma ine sindinasiye kutsatira malamulo anu.

88 Ndithandizeni kuti ndikhalebe ndi moyo chifukwa cha chikondi chanu chokhulupirika,

Kuti ndisunge zikumbutso zimene mwatipatsa.

ל [Lamed]

89 Inu Yehova, mawu anu adzakhazikika kumwamba,+

Mpaka kalekale.

90 Kukhulupirika kwanu kudzakhalapobe ku mibadwo yonse.+

Mwakhazikitsa mwamphamvu dziko lapansi, kuti lipitirizebe kukhalapo.+

91 Ntchito zanu zilipobe mpaka pano chifukwa cha zigamulo zanu,

Chifukwa zonsezo zimakutumikirani.

92 Ndikanakhala kuti sindimakonda kwambiri chilamulo chanu,

Ndikanakhala nditafa chifukwa cha mavuto anga.+

93 Sindidzaiwala malamulo anu,

Chifukwa mwandithandiza kuti ndikhalebe ndi moyo pogwiritsa ntchito malamulo amenewo.+

94 Ine ndine wanu. Chonde ndipulumutseni,+

Chifukwa ndimayesetsa kuphunzira malamulo anu.+

95 Oipa amayembekezera kuti andiwononge,

Koma ine ndimamvetsera mwatcheru zikumbutso zanu.

96 Ndaona kuti zinthu zonse zabwino kwambiri zili ndi malire,

Koma malamulo anu alibe malire.*

מ [Mem]

97 Ndimakonda kwambiri chilamulo chanu!+

Ndimaganizira mozama* chilamulocho tsiku lonse.+

98 Malamulo anu amandichititsa kukhala wanzeru kuposa adani anga,+

Chifukwa ali ndi ine mpaka kalekale.

99 Ndine wozindikira kwambiri kuposa aphunzitsi anga onse,+

Chifukwa ndimaganizira mozama* zikumbutso zanu.

100 Ndimachita zinthu mozindikira kuposa anthu achikulire,

Chifukwa ndimatsatira malamulo anu.

101 Ndimakana kuyenda mʼnjira iliyonse yoipa,+

Kuti ndisunge mawu anu.

102 Sindinasiye kutsatira zigamulo zanu,

Chifukwa inu mwandilangiza.

103 Mawu anu amatsekemera kwambiri mʼkamwa mwanga,

Kuposa mmene uchi umakomera!+

104 Ndimachita zinthu mozindikira chifukwa cha malamulo anu.+

Nʼchifukwa chake ndimadana ndi njira iliyonse yachinyengo.+

נ [Nun]

105 Mawu anu ndi nyale younikira kumapazi anga,

Komanso kuwala kounikira njira yanga.+

106 Ndalumbira kuti ndidzasunga zigamulo zanu zolungama,

Ndipo ndidzakwaniritsa lumbiro langa.

107 Ndavutika kwambiri.+

Inu Yehova, ndithandizeni kuti ndikhalebe ndi moyo mogwirizana ndi mawu anu.+

108 Inu Yehova, chonde sangalalani ndi nsembe zanga zaufulu zokutamandani,*+

Ndipo mundiphunzitse zigamulo zanu.+

109 Nthawi zonse moyo wanga umakhala pangozi,*

Koma sindinaiwale chilamulo chanu.+

110 Oipa anditchera msampha,

Koma ine sindinasochere nʼkusiya kutsatira malamulo anu.+

111 Ndimaona kuti zikumbutso zanu ndi chuma changa mpaka kalekale,*

Chifukwa zimasangalatsa mtima wanga.+

112 Ndatsimikiza mtima kumvera malamulo anu

Nthawi zonse, mpaka ndidzamwalire.

ס [Samekh]

113 Ndimadana ndi anthu amitima iwiri,+

Koma ndimakonda chilamulo chanu.+

114 Inu ndinu malo anga obisalamo komanso chishango changa,+

Chifukwa mawu anu ndi chiyembekezo changa.*+

115 Mukhale kutali ndi ine, anthu oipa inu,+

Kuti ndisunge malamulo a Mulungu wanga.

116 Inu Mulungu, ndithandizeni mogwirizana ndi zimene munalonjeza,*+

Kuti ndikhalebe ndi moyo.

Musalole kuti ndichite manyazi chifukwa cha chiyembekezo changa.*+

117 Ndithandizeni kuti ndipulumutsidwe.+

Mukatero ndidzamvera malangizo anu nthawi zonse.+

118 Onse amene amasochera nʼkusiya kutsatira malangizo anu mumawakana,+

Chifukwa ndi abodza komanso achinyengo.

119 Anthu onse oipa apadziko lapansi mumawataya ngati zinthu zopanda ntchito zimene zimatsalira poyenga zitsulo.+

Nʼchifukwa chake ine ndimakonda zikumbutso zanu.

120 Chifukwa choopa inu, thupi langa limanjenjemera.

Ndikuopa zigamulo zanu.

ע [Ayin]

121 Ndachita zinthu zachilungamo komanso zoyenera.

Musandipereke kwa anthu amene amandipondereza.

122 Lonjezani kuti mudzandithandiza ine mtumiki wanu.

Musalole kuti anthu odzikuza andipondereze.

123 Maso anga afooka chifukwa choyembekezera chipulumutso chanu+

Komanso malonjezo* anu olungama.+

124 Ndisonyezeni chikondi chanu chokhulupirika ine mtumiki wanu,+

Ndipo ndiphunzitseni malamulo anu.+

125 Ine ndine mtumiki wanu. Ndithandizeni kukhala wozindikira,+

Kuti ndidziwe zikumbutso zanu.

126 Nthawi yoti Yehova achitepo kanthu yakwana,+

Chifukwa iwo aphwanya chilamulo chanu.

127 Nʼchifukwa chake ine ndimakonda malamulo anu

Kuposa golide, ngakhale golide wabwino kwambiri.*+

128 Choncho ndimaona kuti malangizo* onse ochokera kwa inu ndi abwino.+

Ndimadana ndi njira iliyonse yachinyengo.+

פ [Pe]

129 Zikumbutso zanu nʼzodabwitsa.

Nʼchifukwa chake ine ndimazitsatira.

130 Mawu anu akafotokozedwa amathandiza munthu kuti akhale wozindikira,+

Amathandiza munthu wosadziwa zambiri kuti akhale wozindikira.+

131 Ndatsegula kwambiri pakamwa panga kuti ndiuse moyo,*

Chifukwa ndikulakalaka malamulo anu.+

132 Ndiyangʼaneni ndipo mundikomere mtima,+

Mogwirizana ndi zigamulo zimene mumapereka kwa anthu amene amakonda dzina lanu.+

133 Nditsogolereni ndi mawu anu kuti ndiyende mʼnjira yotetezeka.

Musalole kuti choipa chilichonse chindilamulire.+

134 Ndipulumutseni* kwa anthu amene akundipondereza,

Ndipo ine ndidzasunga malamulo anu.

135 Chititsani nkhope yanu kuti indiwalire* ine mtumiki wanu,+

Ndipo mundiphunzitse malamulo anu.

136 Misozi ikutsika mʼmaso mwanga ngati mtsinje

Chifukwa anthu sakusunga chilamulo chanu.+

צ [Tsade]

137 Ndinu wolungama, inu Yehova,+

Ndipo zigamulo zanu ndi zachilungamo.+

138 Zikumbutso zimene mumapereka ndi zolungama

Komanso nʼzodalirika kwambiri.

139 Kudzipereka kwanga kwa inu kuli ngati moto umene ukuyaka mumtima mwanga,+

Chifukwa adani anga aiwala mawu anu.

140 Mawu anu ndi oyengeka bwino kwambiri,+

Ndipo ine mtumiki wanu ndimawakonda.+

141 Anthu ena amandiona ngati wopanda ntchito komanso wonyozeka.+

Komabe sindinaiwale malamulo anu.

142 Chilungamo chanu chidzakhalapo mpaka kalekale,+

Ndipo chilamulo chanu ndi choonadi.+

143 Ngakhale kuti ndikukumana ndi zowawa komanso mavuto,

Ndikupitirizabe kukonda malamulo anu.

144 Zikumbutso zanu zidzakhalabe zolungama mpaka kalekale.

Ndithandizeni kukhala wozindikira+ kuti ndikhalebe ndi moyo.

ק [Qoph]

145 Ndaitana ndi mtima wanga wonse. Ndiyankheni inu Yehova.

Ndidzatsatira malangizo anu.

146 Ndakuitanani. Ndipulumutseni chonde!

Ndidzasunga zikumbutso zanu.

147 Ndadzuka mʼbandakucha kuti ndipemphe thandizo kwa inu,+

Chifukwa mawu anu ndi chiyembekezo changa.*

148 Ndimadzuka pakati pa usiku,*

Kuti ndiganizire mozama* mawu anu.+

149 Imvani mawu anga chifukwa cha chikondi chanu chokhulupirika.+

Inu Yehova, ndithandizeni kuti ndikhalebe ndi moyo mogwirizana ndi chilungamo chanu.

150 Anthu amene amakonda kuchita khalidwe lochititsa manyazi* abwera pafupi ndi ine.

Iwo ndi otalikirana kwambiri ndi chilamulo chanu.

151 Inu Yehova muli pafupi,+

Ndipo malamulo anu onse ndi choonadi.+

152 Kale kwambiri, ndinaphunzira zokhudza zikumbutso zanu,

Kuti munazikhazikitsa kuti zikhalepo mpaka kalekale.+

ר [Resh]

153 Onani mavuto anga ndipo mundipulumutse,+

Chifukwa sindinaiwale chilamulo chanu.

154 Nditetezeni pa mlandu wanga* ndipo mundipulumutse.+

Ndithandizeni kuti ndikhalebe ndi moyo mogwirizana ndi lonjezo lanu.*

155 Chipulumutso chili kutali kwambiri ndi anthu oipa,

Chifukwa sanaphunzire malamulo anu.+

156 Chifundo chanu nʼchachikulu, inu Yehova.+

Ndithandizeni kuti ndikhalebe ndi moyo mogwirizana ndi chilungamo chanu.

157 Anthu ondizunza komanso adani anga ndi ambiri.+

Koma ine sindinasiye kutsatira zikumbutso zanu.

158 Ndimanyansidwa ndi anthu ochita zinthu mwachinyengo,

Chifukwa sasunga mawu anu.+

159 Onani mmene ndimakondera malamulo anu.

Inu Yehova, ndithandizeni kuti ndikhalebe ndi moyo chifukwa cha chikondi chanu chokhulupirika.+

160 Mawu anu onse ndi choonadi chokhachokha,+

Ndipo zigamulo zanu zonse zolungama zidzakhalapo mpaka kalekale.

ש [Sin] kapena kuti [Shin]

161 Akalonga amandizunza+ popanda chifukwa,

Koma mtima wanga umaopa mawu anu.+

162 Ndimasangalala ndi mawu anu,+

Mofanana ndi munthu amene wapeza chuma chambiri.

163 Ndimadana ndi chinyengo ndipo chimandinyansa,+

Ndimakonda chilamulo chanu.+

164 Ndimakutamandani maulendo 7 pa tsiku,

Chifukwa cha zigamulo zanu zolungama.

165 Anthu amene amakonda chilamulo chanu amakhala ndi mtendere wochuluka,+

Palibe chimene chingawakhumudwitse.*

166 Ndimayembekezera ntchito zanu zachipulumutso, inu Yehova,

Ndipo ndimatsatira malamulo anu.

167 Ndimasunga zikumbutso zanu,

Ndipo ndimazikonda kwambiri.+

168 Ndimasunga malamulo anu ndi zikumbutso zanu,

Chifukwa inu mukudziwa zinthu zonse zimene ndimachita.+

ת [Taw]

169 Inu Yehova, imvani kulira kwanga kopempha thandizo.+

Ndithandizeni kuti ndikhale wozindikira, mogwirizana ndi mawu anu.+

170 Pempho langa lakuti mundikomere mtima lifike kwa inu.

Ndipulumutseni mogwirizana ndi zimene munalonjeza.*

171 Milomo yanga isefukire ndi mawu okutamandani,+

Chifukwa mumandiphunzitsa malamulo anu.

172 Lilime langa liimbe zokhudza mawu anu,+

Chifukwa malamulo anu onse ndi olungama.

173 Dzanja lanu likhale lokonzeka kundithandiza,+

Chifukwa ndasankha kumvera malamulo anu.+

174 Ndikulakalaka chipulumutso chanu, inu Yehova,

Ndipo ndimakonda kwambiri chilamulo chanu.+

175 Ndithandizeni kuti ndikhale ndi moyo kuti ndikutamandeni,+

Zigamulo zanu zindithandize.

176 Ndasochera ngati nkhosa yotayika.+ Ndifunefuneni ine mtumiki wanu,

Chifukwa sindinaiwale malamulo anu.+

Nyimbo Yokwerera Kumzinda.*

120 Nditakumana ndi mavuto ndinafuulira Yehova,+

Ndipo iye anandiyankha.+

 2 Inu Yehova, ndipulumutseni ku milomo yonama

Komanso ku lilime lachinyengo.

 3 Iwe lilime lachinyengo,+

Kodi Mulungu adzakuchitira chiyani ndipo adzakupatsa chilango chotani?*

 4 Adzakulanga pogwiritsa ntchito mivi yakuthwa+ ya msilikali

Komanso makala amoto+ a mtengo wamʼchipululu.

 5 Tsoka kwa ine, chifukwa ndakhala mʼdziko la Meseki+ ngati mlendo.

Ndimakhala mutenti pakati pa matenti a ku Kedara.+

 6 Ndakhala kwa nthawi yaitali

Limodzi ndi anthu odana ndi mtendere.+

 7 Ine ndimakonda mtendere, koma ndikalankhula

Iwo amafuna nkhondo.

Nyimbo Yokwerera Kumzinda.

121 Ndakweza maso anga kuyangʼana kumapiri.+

Kodi thandizo langa lichokera kuti?

 2 Thandizo langa limachokera kwa Yehova,+

Amene anapanga kumwamba ndi dziko lapansi.

 3 Iye sadzalola kuti phazi lako literereke.*+

Amene akukuyangʼanira sadzawodzera.

 4 Taonani! Amene akuyangʼanira Isiraeli,+

Sadzawodzera kapena kugona.

 5 Yehova akukuyangʼanira.

Yehova ndi mthunzi+ wako kudzanja lako lamanja.+

 6 Masana dzuwa silidzakupweteka,+

Kapenanso mwezi usiku.+

 7 Yehova adzakuteteza ku zinthu zonse zimene zingakuvulaze.+

Iye adzateteza moyo wako.+

 8 Yehova adzakuteteza pa zochita zako zonse,*

Kuyambira panopa mpaka kalekale.

Nyimbo Yokwerera Kumzinda. Salimo la Davide.

122 Ndinasangalala pamene anandiuza kuti:

“Tiyeni tipite kunyumba ya Yehova.”+

 2 Ndipo tsopano mapazi athu aima

Pamageti ako iwe Yerusalemu.+

 3 Yerusalemu ndi mzinda umene wamangidwa

Ngati chinthu chimodzi chogwirizana.+

 4 Mafuko apita kumeneko,

Mafuko a Ya,*

Mogwirizana ndi chilamulo chimene* Isiraeli anapatsidwa

Kuti azikatamanda dzina la Yehova.+

 5 Chifukwa kumeneko nʼkumene kunaikidwa mipando yachiweruzo,+

Mipando yachifumu ya nyumba ya Davide.+

 6 Pemphererani mtendere wa Yerusalemu.+

Amene amakukonda, mzinda iwe, adzakhala otetezeka.

 7 Mtendere upitirize kukhala mʼmalo ako otchingidwa ndi mpanda wolimba,

Chitetezo chipitirize kukhala munsanja zako zokhala ndi mpanda wolimba.

 8 Chifukwa choti ndimakonda abale anga komanso anzanga ndikunena kuti:

“Mumzindawu mukhale mtendere.”

 9 Chifukwa choti ndimakonda nyumba ya Yehova Mulungu wathu,+

Ndidzapitiriza kukufunira zabwino.

Nyimbo Yokwerera Kumzinda.

123 Ndakweza maso anga kuyangʼana inu,+

Inu amene mpando wanu wachifumu uli kumwamba.

 2 Mofanana ndi mmene maso a atumiki amayangʼanira dzanja la mbuye wawo,

Komanso mmene maso a kapolo wamkazi amayangʼanira dzanja la mbuye wake wamkazi,

Maso athu akuyangʼana kwa Yehova Mulungu wathu,+

Mpakana atatikomera mtima.+

 3 Tikomereni mtima, inu Yehova, tikomereni mtima,

Chifukwa tanyozeka kwambiri.+

 4 Anthu odzikuza atinyoza kwambiri*

Ndipo anthu onyada atichitira zachipongwe.

Nyimbo Yokwerera Kumzinda. Salimo la Davide.

124 “Yehova akanapanda kukhala nafe,”+

Tsopano Isiraeli anene kuti,

 2 “Yehova akanapanda kukhala nafe,+

Pamene anthu anatiukira,+

 3 Akanatimeza amoyo+

Pamene mkwiyo wawo unatiyakira.+

 4 Pamenepo madzi akanatikokolola,

Mtsinje wamphamvu ukanatimiza.+

 5 Madzi amphamvu akanatikokolola.

 6 Yehova atamandike,

Chifukwa sanatipereke kwa iwo kuti atimbwandire ngati nyama.

 7 Tili ngati mbalame imene yathawa

Pamsampha wa munthu wosaka.+

Msamphawo unathyoka,

Ndipo ife tinathawa.+

 8 Thandizo lathu lili mʼdzina la Yehova,+

Amene anapanga kumwamba ndi dziko lapansi.”

Nyimbo Yokwerera Kumzinda.

125 Anthu amene amakhulupirira Yehova+

Ali ngati phiri la Ziyoni, limene silingagwedezeke

Koma lidzakhalapo mpaka kalekale.+

 2 Mofanana ndi mapiri amene azungulira Yerusalemu,+

Yehova wazungulira anthu ake,+

Kuyambira panopa mpaka kalekale.

 3 Ndodo yachifumu ya oipa sidzapitiriza kukhala padziko limene laperekedwa kwa anthu olungama,+

Kuti olungamawo* asayambe kuchita zinthu zoipa.+

 4 Inu Yehova, anthu abwino muwachitire zabwino,+

Muchitire zabwino anthu owongoka mtima.+

 5 Koma anthu amene apatuka panjira yabwino nʼkuyamba kuyenda mʼnjira zokhotakhota,

Yehova adzawachotsa limodzi ndi anthu ochita zoipa.+

Mu Isiraeli mukhale mtendere.

Nyimbo Yokwerera Kumzinda.

126 Yehova atabwezeretsa anthu a ku Ziyoni kuchokera ku ukapolo,+

Tinkangoona ngati tikulota.

 2 Pa nthawiyo tinaseka

Ndipo tinasangalala kwambiri.+

Pa nthawi imeneyo anthu a mitundu ina anayamba kuuzana kuti:

“Yehova wachitira anthu amenewa zinthu zazikulu.”+

 3 Yehova watichitira zazikulu,+

Ndipo tasangalala kwambiri.

 4 Inu Yehova, bwezeretsani anthu athu amene anagwidwa ukapolo,

Ngati mmene mvula imadzazitsira mitsinje ya ku Negebu.*

 5 Amene akukhetsa misozi pofesa mbewu

Adzakolola akufuula mosangalala.

 6 Amene akupitabe kumunda, ngakhale kuti akulira,

Atasenza thumba lake la mbewu,

Ndithu adzabwerako akufuula mosangalala,+

Atasenza mtolo wake wa zokolola.+

Nyimbo Yokwerera Kumzinda. Salimo la Solomo.

127 Yehova akapanda kumanga nyumba,

Omanga nyumbayo amagwira ntchito pachabe.+

Yehova akapanda kulondera mzinda,+

Alonda amakhala maso pachabe.

 2 Mukudzuka mʼmawa pachabe,

Mukungovutika kugwira ntchito mpaka usiku,

Mumapeza chakudya movutikira,

Chifukwa Mulungu amapereka zinthu zofunika kwa anthu amene amawakonda komanso amawapatsa tulo tabwino.+

 3 Taonani! Ana ndi cholowa chochokera kwa Yehova.+

Chipatso cha mimba ndi mphoto yochokera kwa Mulungu.+

 4 Ana a bambo wachinyamata,+

Ali ngati mivi mʼdzanja la mwamuna wamphamvu.

 5 Wosangalala ndi mwamuna amene wadzaza kachikwama kake ka mivi ndi mivi imeneyo.+

Abambo oterowo sadzachita manyazi,

Chifukwa ana awo adzalankhula ndi adani pageti la mzinda.

Nyimbo Yokwerera Kumzinda.

128 Wosangalala ndi aliyense amene amaopa Yehova,+

Amene amayenda mʼnjira za Mulungu.+

 2 Udzadya zinthu zimene wapeza utagwira ntchito mwakhama.

Udzakhala wosangalala ndipo zinthu zidzakuyendera bwino.+

 3 Mkazi wako adzakhala ngati mtengo wa mpesa wobereka zipatso mʼnyumba mwako.+

Ana ako adzakhala ngati mphukira za mtengo wa maolivi kuzungulira tebulo lako.

 4 Mwamuna aliyense amene amaopa Yehova

Adzadalitsidwa mwa njira imeneyi.+

 5 Yehova adzakudalitsa ali ku Ziyoni.

Uone zinthu zikuyenda bwino mu Yerusalemu masiku onse a moyo wako,+

 6 Ndipo uone ana a ana ako.

Mtendere ukhale pa Isiraeli.

Nyimbo Yokwerera Kumzinda.

129 “Akhala akundiukira nthawi zonse kuyambira ndili mnyamata,”+

Tsopano Isiraeli anene kuti,

 2 “Akhala akundiukira nthawi zonse kuyambira ndili mnyamata,+

Koma sanandigonjetse.+

 3 Olima ndi ngʼombe andilima pamsana.+

Iwo alima mizere italiitali.”

 4 Koma Yehova ndi wolungama.+

Iye wadula zingwe za oipa.+

 5 Onse amene amadana ndi Ziyoni,

Adzanyozeka ndipo adzabwerera mwamanyazi.+

 6 Adzakhala ngati udzu umene wamera padenga

Umene umauma usanazulidwe,

 7 Umene sungadzaze mʼdzanja la munthu amene akukolola

Kapena mʼmanja mwa munthu amene akumanga mitolo ya zokolola.

 8 Anthu odutsa sadzanena kuti:

“Madalitso a Yehova akhale nanu.

Tikukudalitsani mʼdzina la Yehova.”

Nyimbo Yokwerera Kumzinda.

130 Inu Yehova, pa nthawi imene zinthu zinandivuta kwambiri ndinaitana pa inu.+

 2 Inu Yehova, imvani mawu anga.

Makutu anu amve kuchonderera kwanga kopempha thandizo.

 3 Inu Ya,* mukanakhala kuti mumayangʼanitsitsa* zolakwa,

Ndi ndani akanaima pamaso panu, inu Yehova?+

 4 Chifukwa inu mumakhululuka ndi mtima wonse,+

Kuti anthu azikuopani.+

 5 Ndikuyembekezera Yehova. Moyo wanga wonse ukumuyembekezera.

Ine ndikuyembekezera mawu ake.

 6 Ndikuyembekezera Yehova ndi mtima wonse,+

Kuposa alonda amene akuyembekezera kuti kuche,+

Ndithu kuposa alonda amene akuyembekezera kuti kuche.

 7 Isiraeli apitirize kuyembekezera Yehova,

Chifukwa Yehova amasonyeza chikondi chokhulupirika,+

Ndipo ali ndi mphamvu zochuluka zowombolera anthu.

 8 Iye adzawombola Aisiraeli ku zolakwa zawo zonse.

Nyimbo Yokwerera Kumzinda. Salimo la Davide.

131 Inu Yehova, mtima wanga si wodzikweza,

Maso anga si onyada.+

Sindilakalaka zinthu zapamwamba kwambiri,+

Kapena zinthu zimene sindingazikwanitse.

 2 Koma ine ndatonthoza mtima wanga ndipo ndaukhazika mʼmalo+

Ngati mwana amene anamusiyitsa kuyamwa, amene ali mʼmanja mwa mayi ake.

Ndine wokhutira ngati mwana amene anamusiyitsa kuyamwa.

 3 Isiraeli ayembekezere Yehova,+

Kuyambira panopa mpaka kalekale.

Nyimbo Yokwerera Kumzinda.

132 Inu Yehova, kumbukirani Davide

Komanso mavuto onse amene anakumana nawo.+

 2 Kumbukirani kuti analumbira kwa inu Yehova,

Analonjeza kwa Wamphamvu wa Yakobo kuti:+

 3 “Sindidzalowa mutenti yanga, mʼnyumba yanga.+

Sindidzagona pabedi langa.

 4 Sindidzalola kuti ndigone

Kapena kutseka maso anga,

 5 Mpaka nditamupezera Yehova malo okhala,

Malo abwino oti* Wamphamvu wa Yakobo azikhalamo.”+

 6 Ku Efurata,+ tinamva zimene zinachitika.

Tinalipeza kunkhalango.*+

 7 Tiyeni tilowe mʼmalo ake okhala.*+

Tiyeni tiwerame pachopondapo mapazi ake.+

 8 Nyamukani, inu Yehova, kuti mulowe mʼmalo anu okhalamo,+

Inu pamodzi ndi Likasa limene likuimira mphamvu zanu.+

 9 Ansembe anu avale chilungamo,

Ndipo okhulupirika anu afuule mosangalala.

10 Chifukwa cha zimene munalonjeza Davide mtumiki wanu,

Musakane* wodzozedwa wanu.+

11 Yehova walumbira kwa Davide.

Ndithudi sadzalephera kukwaniritsa mawu ake akuti:

“Ndidzaika pampando wako wachifumu

Mmodzi wa ana ako.*+

12 Ana ako akadzasunga pangano langa

Komanso malamulo* anga amene ndikuwaphunzitsa,+

Ana awonso

Adzakhala pampando wako wachifumu kwamuyaya.”+

13 Chifukwa Yehova wasankha Ziyoni.+

Akufunitsitsa kuti akhale malo ake okhalamo. Iye akuti:+

14 “Awa ndi malo anga okhalamo mpaka kalekale.

Ndidzakhala mmenemu,+ chifukwa zimenezi ndi zimene ndikulakalaka.

15 Ndidzadalitsa kwambiri malo amenewa ndi chakudya.

Anthu ake osauka ndidzawapatsa chakudya chokwanira.+

16 Ansembe ake ndidzawaveka chipulumutso,+

Ndipo okhulupirika ake adzafuula mosangalala.+

17 Kumeneko ndidzachulukitsa mphamvu* za Davide.

Wodzozedwa wanga ndamukonzera nyale.+

18 Adani ake ndidzawaveka manyazi,

Koma ufumu wake udzakhala wamphamvu.”*+

Nyimbo Yokwerera Kumzinda. Salimo la Davide.

133 Taonani! Ndi zabwino komanso zosangalatsa kwambiri

Abale akakhala pamodzi mogwirizana!+

 2 Zili ngati mafuta abwino amene athiridwa pamutu+

Amene akuyenderera pandevu,

Ndevu za Aroni,+

Ndipo akuyenderera mpaka mʼkolala ya zovala zake.

 3 Zili ngati mame a ku Herimoni,+

Amene akutsikira pamapiri a ku Ziyoni.+

Kumeneko nʼkumene Yehova analonjeza kuti kudzakhala madalitso ake,

Omwe ndi moyo wosatha.

Nyimbo Yokwerera Kumzinda.

134 Tamandani Yehova,

Inu nonse atumiki a Yehova,+

Inu amene mumaimirira mʼnyumba ya Yehova usiku.+

 2 Muzikhala oyera mukamapemphera mutakweza manja anu*+

Ndipo muzitamanda Yehova.

 3 Yehova, amene anapanga kumwamba ndi dziko lapansi,

Akudalitseni ali ku Ziyoni.

135 Tamandani Ya!*

Tamandani dzina la Yehova,

Mutamandeni, inu atumiki a Yehova,+

 2 Inu amene mwaimirira mʼnyumba ya Yehova,

Mʼmabwalo a nyumba ya Mulungu wathu.+

 3 Tamandani Ya, chifukwa Yehova ndi wabwino.+

Muimbireni nyimbo zotamanda dzina lake, chifukwa kuchita zimenezi nʼkosangalatsa.

 4 Ya wasankha Yakobo kuti akhale wake,

Wasankha Isiraeli kuti akhale chuma chake chapadera.*+

 5 Ine ndikudziwa bwino kuti Yehova ndi wamkulu.

Ambuye wathu ndi wamkulu kuposa milungu ina yonse.+

 6 Yehova amachita chilichonse chimene wafuna+

Kumwamba, padziko lapansi, mʼnyanja komanso mʼmalo onse ozama.

 7 Amachititsa kuti mitambo* ikwere kuchokera kumalekezero a dziko lapansi.

Iye amachititsa kuti kukamagwa mvula mphezi zizingʼanima.

Amatulutsa mphepo kuchokera mʼnyumba zake zosungira zinthu.+

 8 Iye anapha ana oyamba kubadwa a ku Iguputo,

Ana a anthu komanso ana a nyama.+

 9 Anachita zizindikiro komanso zodabwitsa pakati pako, iwe Iguputo,+

Anachita zimenezi kwa Farao ndi kwa atumiki ake onse.+

10 Anawononga mitundu yambiri+

Ndipo anapha mafumu amphamvu+

11 Anapha Sihoni mfumu ya Aamori,+

Ogi mfumu ya Basana+

Komanso anawononga maufumu onse a ku Kanani.

12 Dziko lawo analipereka kuti likhale cholowa,

Cholowa cha anthu ake Aisiraeli.+

13 Inu Yehova, dzina lanu lidzakhalapo kwamuyaya.

Inu Yehova, dzina lanu lidzakhalapo* ku mibadwo yonse.+

14 Chifukwa Yehova adzateteza anthu ake pa mlandu,*+

Ndipo adzamvera chisoni atumiki ake.+

15 Mafano a anthu a mitundu ina ndi opangidwa ndi siliva komanso golide,

Ntchito ya manja a anthu.+

16 Pakamwa ali napo koma sangalankhule.+

Maso ali nawo koma sangaone.

17 Makutu ali nawo koma sangamve.

Mʼkamwa mwawo mulibe mpweya.+

18 Anthu amene amawapanga adzafanana nawo,+

Chimodzimodzinso anthu onse amene amakhulupirira mafanowo.+

19 Inu nyumba ya Isiraeli, tamandani Yehova.

Inu nyumba ya Aroni, tamandani Yehova.

20 Inu nyumba ya Levi, tamandani Yehova.+

Inu amene mumaopa Yehova, tamandani Yehova.

21 Yehova amene akukhala ku Yerusalemu,+

Atamandidwe mu Ziyoni.+

Tamandani Ya!+

136 Yamikani Yehova, chifukwa iye ndi wabwino.+

Chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale.+

 2 Yamikani Mulungu wa milungu,+

Chifukwa chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale.

 3 Yamikani Mbuye wa ambuye,

Chifukwa chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale.

 4 Iye yekha ndi amene amachita ntchito zazikulu zodabwitsa,+

Chifukwa chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale.+

 5 Iye anapanga kumwamba mwaluso,*+

Chifukwa chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale.

 6 Anayala dziko lapansi pamwamba pa madzi,+

Chifukwa chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale.

 7 Iye anapanga zounikira zazikulu,+

Chifukwa chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale.

 8 Anapanga dzuwa kuti lizilamulira masana,+

Chifukwa chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale.

 9 Anapanga mwezi ndi nyenyezi kuti zizilamulira usiku,+

Chifukwa chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale.

10 Iye anapha ana oyamba kubadwa a Aiguputo,+

Chifukwa chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale.

11 Iye anatulutsa Aisiraeli pakati pawo,+

Chifukwa chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale,

12 Anawatulutsa ndi dzanja lamphamvu+ komanso mkono wotambasula,

Chifukwa chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale.

13 Iye anagawa pakati Nyanja Yofiira,+

Chifukwa chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale.

14 Anachititsa kuti Isiraeli adutse pakati pake,+

Chifukwa chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale.

15 Anakutumulira Farao ndi asilikali ake mʼNyanja Yofiira,+

Chifukwa chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale.

16 Iye anatsogolera anthu ake mʼchipululu,+

Chifukwa chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale.

17 Anapha mafumu akuluakulu,+

Chifukwa chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale.

18 Anapha mafumu amphamvu,

Chifukwa chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale,

19 Sihoni+ mfumu ya Aamori,

Chifukwa chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale,

20 Komanso Ogi+ mfumu ya Basana,

Chifukwa chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale.

21 Iye anapereka dziko lawo kwa anthu ake kuti likhale cholowa,+

Chifukwa chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale,

22 Kuti likhale cholowa cha Isiraeli mtumiki wake,

Chifukwa chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale.

23 Iye anatikumbukira pa nthawi imene tinali ofooka,+

Chifukwa chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale.+

24 Anapitiriza kutipulumutsa kwa adani athu,+

Chifukwa chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale.

25 Amapereka chakudya kwa zamoyo zonse,+

Chifukwa chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale.

26 Yamikani Mulungu wakumwamba,

Chifukwa chikondi chake chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale.

137 Tinakhala pansi mʼmphepete mwa mitsinje ya ku Babulo.+

Tinalira titakumbukira Ziyoni.+

 2 Tinapachika azeze athu+

Pamitengo ya msondodzi imene inali mmenemo.*

 3 Chifukwa kumeneko, anthu amene anatigwira ukapolo anatiuza kuti tiwaimbire nyimbo,+

Amene ankatinyozawo ankafuna kuti tiwasangalatse. Iwo anati:

“Tiimbireni nyimbo imodzi ya ku Ziyoni.”

 4 Tingaimbe bwanji nyimbo ya Yehova

Mʼdziko lachilendo?

 5 Ndikakuiwala iwe Yerusalemu,

Dzanja langa lamanja liiwale luso lake.+

 6 Lilime langa limamatire mʼkamwa mwanga

Ngati sindingakukumbukire,

Ngati sindingaike Yerusalemu pamwamba

Pa chilichonse chimene chimandisangalatsa kwambiri.+

 7 Inu Yehova, kumbukirani

Zimene Aedomu ananena pa tsiku limene Yerusalemu anawonongedwa.

Iwo anati: “Gwetsani mzindawo! Ugwetseni mpaka pamaziko ake!”+

 8 Iwe mwana wamkazi wa Babulo,* amene watsala pangʼono kuwonongedwa,+

Wosangalala adzakhala amene adzakubwezere

Zimene iwe watichitira.+

 9 Wosangalala adzakhala amene adzagwire ana ako

Nʼkuwaphwanya powawombetsa pathanthwe.+

Salimo la Davide.

138 Ndidzakutamandani ndi mtima wanga wonse.+

Ndidzakuimbirani nyimbo zokutamandani

Pamaso pa milungu ina.

 2 Ndidzawerama nditayangʼana kukachisi wanu woyera,*+

Ndipo ndidzatamanda dzina lanu+

Chifukwa cha kukhulupirika kwanu ndiponso chikondi chanu chokhulupirika.

Chifukwa mwasonyeza kuti dzina lanu komanso malonjezo anu ndi apamwamba kuposa china chilichonse.*

 3 Pa tsiku limene ine ndinaitana, inu munandiyankha.+

Munandilimbitsa mtima komanso kundipatsa mphamvu.+

 4 Mafumu onse apadziko lapansi adzakutamandani, inu Yehova,+

Chifukwa adzakhala atamva malonjezo amene mwanena.

 5 Iwo adzaimba zokhudza njira za Yehova,

Chifukwa ulemerero wa Yehova ndi waukulu.+

 6 Ngakhale kuti Yehova ali pamwamba, amaona wodzichepetsa,+

Koma wonyada samuyandikira.+

 7 Ngakhale nditakumana ndi mavuto, inu mudzandithandiza kuti ndikhalebe ndi moyo.+

Mumagwiritsa ntchito mphamvu zanu polimbana ndi adani anga omwe ndi okwiya.

Dzanja lanu lamanja lidzandipulumutsa.

 8 Yehova adzakwaniritsa zolinga zimene ali nazo pa ine.

Inu Yehova, chikondi chanu chokhulupirika chidzakhalapo mpaka kalekale.+

Musasiye ntchito ya manja anu.+

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ndi Salimo la Davide.

139 Inu Yehova, mwandifufuza ndipo mukundidziwa.+

 2 Inu mumadziwa ndikakhala pansi komanso ndikaimirira.+

Mumadziwa maganizo anga muli kutali.+

 3 Mumandiona* ndikamayenda komanso ndikagona.

Mumadziwa chilichonse chimene ndikuchita.+

 4 Ndisananene kanthu,

Inu Yehova mumakhala mutadziwa kale zonse.+

 5 Mwandizungulira mbali zonse,

Ndipo mwaika dzanja lanu pa ine.

 6 Kwa ine nʼzovuta kwambiri kuti ndimvetse zinthu zimenezi.*

Ndi zapamwamba kwambiri moti sindingathe kuzifikira.+

 7 Kodi ndingapite kuti kuthawa mzimu wanu,

Ndipo ndingapite kuti kuthawa nkhope yanu?+

 8 Ngati ndingakwere kumwamba, inu mudzakhala komweko,

Ndipo ngati ndingayale bedi langa ku Manda,* taonani! inunso mudzakhala komweko.+

 9 Ngati ndingauluke pamapiko amʼbandakucha

Kuti ndikakhale mʼnyanja yakutali kwambiri,

10 Ngakhale kumenekonso dzanja lanu lidzanditsogolera

Ndipo dzanja lanu lamanja lidzandigwira.+

11 Ngati ndinganene kuti: “Ndithudi mdima undibisa!”

Pamenepo mdima umene wandizungulira udzasanduka kuwala.

12 Ngakhale mdimawo sudzakhala mdima wandiweyani kwa inu,

Koma usiku udzawala ngati masana.+

Mdima udzangokhala ngati kuwala kwa inu.+

13 Inu munapanga impso zanga.

Munanditeteza* ndili mʼmimba mwa mayi anga.+

14 Ndimakutamandani chifukwa munandipanga modabwitsa+ ndipo zimenezi zimandichititsa mantha.

Ntchito zanu ndi zodabwitsa,+

Ine ndikudziwa bwino zimenezi.

15 Mafupa anga sanali obisika kwa inu

Pa nthawi imene ndinkapangidwa kumalo amene aliyense sakanatha kuona,

Pamene munkandiwomba ngati nsalu mʼmalo apansi kwambiri padziko lapansi.+

16 Maso anu anandiona ngakhale pamene ndinali mluza.*

Ziwalo zanga zonse zinalembedwa mʼbuku lanu

Mʼbukumo munalembedwa za masiku amene zinapangidwa,

Zinalembedwa chiwalo chilichonse chisanapangidwe.

17 Choncho kwa ine maganizo anu ndi ofunika kwambiri, inu Mulungu,+

Ndipo ndi ochuluka kwambiri.+

18 Nditati ndiyese kuwawerenga, angakhale ochuluka kwambiri kuposa mchenga.+

Podzuka ndingakhale ndikuwawerengabe.*+

19 Inu Mulungu, zikanakhala bwino mukanapha oipa.+

Zikanatero anthu achiwawa* akanachoka kwa ine,

20 Anthu amene amanena zinthu zokhudza inu ndi zolinga zoipa.*

Amenewa ndi adani anu amene amagwiritsa ntchito dzina lanu molakwika.+

21 Inu Yehova, pajatu ine ndimadana ndi anthu amene amadana nanu,+

Ndipo ndimanyansidwa ndi anthu amene amakupandukirani.+

22 Ndimadana nawo kwambiri.+

Kwa ine akhala adani enieni.

23 Ndifufuzeni inu Mulungu, ndipo mudziwe mtima wanga.+

Ndifufuzeni ndipo mudziwe maganizo anga amene akundidetsa nkhawa.*+

24 Muone ngati mwa ine muli chilichonse choipa,+

Ndipo munditsogolere+ mʼnjira yamuyaya.

Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ya Davide.

140 Inu Yehova, ndipulumutseni kwa anthu oipa.

Nditetezeni kwa anthu ochita zachiwawa,+

 2 Anthu amene amakonza chiwembu mʼmitima yawo+

Ndipo amayambitsa mikangano tsiku lonse.

 3 Anola lilime lawo ndipo lakhala ngati la njoka.+

Mʼmilomo yawo muli poizoni wa mphiri.+ (Selah)

 4 Inu Yehova, nditetezeni kuti manja a munthu woipa asandikhudze.+

Nditetezeni kwa anthu amene amachita zachiwawa.

Amene amakonza chiwembu kuti andivulaze.

 5 Anthu onyada anditchera msampha.

Iwo agwiritsa ntchito zingwe kuti atchere ukonde mʼmphepete mwa njira,+

Ndipo anditchera makhwekhwe.+ (Selah)

 6 Ndauza Yehova kuti: “Inu ndinu Mulungu wanga.

Mvetserani inu Yehova, kuchonderera kwanga kopempha thandizo.”+

 7 Inu Yehova Ambuye Wamkulu Koposa, Mpulumutsi wanga wamphamvu,

Mwateteza mutu wanga pa tsiku lankhondo.+

 8 Inu Yehova, musapatse anthu oipa zimene amalakalaka.

Musalole kuti ziwembu zawo zitheke kuti angayambe kunyada.+ (Selah)

 9 Mitu ya anthu amene andizungulira

Iphimbidwe ndi zoipa zimene amalankhula.+

10 Muwakhuthulire makala oyaka moto pamutu pawo.+

Aponyedwe pamoto,

Mʼmaenje akuya*+ ndipo asadzukenso.

11 Munthu wonenera anzake zoipa asapeze malo padziko lapansi.*+

Zoipa zisakesake anthu ochita zachiwawa ndipo ziwawononge.

12 Ndikudziwa kuti Yehova adzateteza anthu onyozeka pa mlandu wawo

Ndipo adzachitira chilungamo anthu osauka.+

13 Ndithudi, anthu olungama adzatamanda dzina lanu.

Anthu owongoka mtima adzakhala pamaso panu.+

Nyimbo ya Davide.

141 Inu Yehova, ine ndakuitanani.+

Bwerani mofulumira kuti mudzandithandize.+

Mutchere khutu ndikamakuitanani.+

 2 Pemphero langa likhale ngati zofukiza+ zokonzedwa pamaso panu,+

Mapembedzero anga akhale ngati nsembe yambewu yamadzulo.+

 3 Inu Yehova, ikani mlonda pakamwa panga.

Ikani woti azilondera patsogolo pa milomo yanga.+

 4 Musalole kuti mtima wanga uzikonda chinthu chilichonse choipa,+

Komanso kuti ndizichita zinthu zoipa limodzi ndi anthu oipa.

Sindikufuna kudya chakudya chawo chapamwamba.

 5 Wolungama akandimenya ndiye kuti wandisonyeza chikondi chokhulupirika.+

Akandidzudzula zingakhale ngati wandidzoza mafuta pamutu,+

Mafuta amene mutu wanga sungawakane.+

Ndidzapemphererabe anthu olungama ngakhale pamene masoka awagwera.

 6 Ngakhale oweruza awo atawagwetsera pansi kuchokera pathanthwe,

Anthu adzamvetsera mawu anga chifukwa ndi osangalatsa.

 7 Mafupa athu amwazika pakamwa pa Manda,*

Mofanana ndi dothi limene limamwazika munthu akamalima.

 8 Koma ine maso anga ali pa inu Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.+

Ine ndathawira kwa inu.

Musachotse moyo wanga.

 9 Nditetezeni kuti ndisagwidwe pamsampha umene anditchera,

Kuti ndisakodwe ndi makhwekhwe a anthu ochita zoipa.

10 Oipa onse adzagwera mʼmaukonde awo omwe,+

Koma ine ndidzadutsa bwinobwino.

Masikili.* Salimo ndiponso pemphero la Davide, pamene anali kuphanga.+

142 Ndimafuulira Yehova kuti andithandize.+

Ndimachonderera Yehova kuti andikomere mtima.

 2 Ndimakhuthula nkhawa zanga pamaso pake.

Ndimafotokoza mavuto anga pamaso pake+

 3 Pamene mphamvu zanga zatha.*

Ndikatero, mumayangʼanitsitsa njira yanga.+

Adani anga anditchera msampha

Mʼnjira imene ndikuyenda.

 4 Yangʼanani kudzanja langa lamanja ndipo muone

Kuti palibe aliyense amene akusamala za ine.*+

Palibenso kulikonse kumene ndingathawire,+

Ndipo palibe amene akundidera nkhawa.

 5 Ndikuitana inu Yehova kuti mundithandize.

Ndikunena kuti: “Inu ndinu malo anga othawirako,+

Malo okhawo amene ndili nawo* mʼdziko la anthu amoyo.”

 6 Mvetserani kulira kwanga kopempha thandizo,

Chifukwa ndavutika kwambiri.

Ndipulumutseni kwa anthu amene akundizunza,+

Chifukwa iwo ndi amphamvu kuposa ine.

 7 Nditulutseni mundende yamdima

Kuti nditamande dzina lanu.

Anthu olungama andizungulire

Chifukwa mumandichitira zabwino.

Nyimbo ya Davide.

143 Inu Yehova, imvani pemphero langa.+

Mvetserani kuchonderera kwanga kopempha thandizo.

Ndiyankheni mogwirizana ndi kukhulupirika kwanu komanso chilungamo chanu.

 2 Musandiimbe mlandu ine mtumiki wanu,

Chifukwa palibe aliyense wamoyo amene angakhale wolungama pamaso panu.+

 3 Mdani akundifunafuna.

Iye wandipondereza ndipo wandigonjetsa.

Wandichititsa kuti ndikhale mumdima ngati anthu amene anafa kalekale.

 4 Mphamvu zanga zatha.*+

Ndipo mtima wanga wachita dzanzi.+

 5 Ndikukumbukira masiku akale.

Ndimaganizira mozama zochita zanu zonse.+

Ndimaganizira* ntchito ya manja anu ndi mtima wonse.

 6 Ine ndikupemphera nditakweza manja anga kwa inu.

Ndikuyembekezera inu ngati dziko louma limene likuyembekezera kuti mvula igwe.+ (Selah)

 7 Ndiyankheni mofulumira, inu Yehova.+

Mphamvu zanga zatha.*+

Musandibisire nkhope yanu,+

Chifukwa mukatero ndikhala ngati anthu amene akutsikira kudzenje la manda.+

 8 Mʼmawa ndichititseni kumva za chikondi chanu chokhulupirika,

Chifukwa ndimadalira inu.

Ndidziwitseni njira imene ndikuyenera kuyendamo,+

Chifukwa ndimadalira inu kuti muzinditsogolera.*

 9 Ndipulumutseni kwa adani anga, inu Yehova.

Ine ndikudalira inu kuti munditeteze.+

10 Ndiphunzitseni kuchita zimene inu mumafuna,+

Chifukwa inu ndinu Mulungu wanga.

Mzimu wanu ndi wabwino.

Unditsogolere mʼmalo otetezeka.*

11 Inu Yehova, ndithandizeni kuti ndikhalebe ndi moyo chifukwa cha dzina lanu.

Ndipulumutseni mʼmavuto anga, chifukwa ndinu wachilungamo.+

12 Chifukwa cha chikondi chanu chokhulupirika, wonongani* adani anga.+

Muwononge onse amene akundichitira nkhanza,+

Chifukwa ine ndine mtumiki wanu.+

Salimo la Davide.

144 Atamandike Yehova Thanthwe langa,+

Amene amaphunzitsa manja anga kumenya nkhondo,

Komanso zala zanga kumenyana ndi adani anga.+

 2 Iye amandisonyeza chikondi chake chokhulupirika ndipo ndi malo anga otetezeka,

Malo anga othawirako otetezeka* komanso amene amandipulumutsa,

Chishango changa ndiponso malo amene ndathawirako kuti nditetezeke,+

Amene amachititsa kuti mitundu ya anthu izindigonjera.+

 3 Inu Yehova, munthu ndi ndani kuti muzimuganizira?

Kodi mwana wa munthu ndi ndani kuti muzimuwerengera?+

 4 Munthu amafanana ndi mpweya.+

Masiku a moyo wake ali ngati mthunzi wongodutsa.+

 5 Inu Yehova, tsitsani* kumwamba ndipo mutsike.+

Khudzani mapiri ndipo muwachititse kuti afuke utsi.+

 6 Chititsani kuti mphezi zingʼanime kuti adani abalalike.+

Ponyani mivi yanu ndipo muwasokoneze.+

 7 Tambasulani manja anu kuchokera kumwamba.

Ndilanditseni ndi kundipulumutsa mʼmadzi amphamvu,

Ndilanditseni mʼmanja mwa anthu achilendo,+

 8 Amene amalankhula zinthu zabodza

Komanso amene amakweza dzanja lawo lamanja kuti alumbire mwachinyengo.*

 9 Inu Mulungu, ine ndidzakuimbirani nyimbo yatsopano.+

Ndidzaimba nyimbo zokutamandani ndi choimbira cha zingwe 10.

10 Ndidzaimbira inu amene mumathandiza mafumu kuti apambane,*+

Inu amene mumapulumutsa Davide mtumiki wanu kuti asaphedwe ndi lupanga.+

11 Ndilanditseni ndi kundipulumutsa mʼmanja mwa anthu achilendo,

Amene amalankhula zinthu zabodza

Komanso amakweza dzanja lawo lamanja kuti alumbire mwachinyengo.

12 Mukatero ana athu aamuna adzakhala ngati mitengo ingʼonoingʼono imene ikukula mofulumira,

Ndipo ana athu aakazi adzakhala ngati zipilala zamʼmakona zosemedwa mwaluso, kuti akazigwiritse ntchito pomanga nyumba yachifumu.

13 Nyumba zathu zosungiramo zinthu zizadzaza ndi zokolola zamitundu yosiyanasiyana.

Nkhosa zathu zidzaswana nʼkukhala masauzandemasauzande kapena masauzande ambirimbiri.

14 Ngʼombe zathu zimene zili ndi bere, sizidzavulala kapena kubereka ana akufa.

Ndipo mʼmabwalo athu simudzamveka kulira kwa munthu amene ali pamavuto.

15 Osangalala ndi anthu amene zimenezi zikuwachitikira.

Osangalala ndi anthu amene Mulungu wawo ndi Yehova.+

Nyimbo ya Davide yotamanda Mulungu.

א [Aleph]

145 Ndidzakukwezani, inu Mfumu ndi Mulungu wanga,+

Ndidzatamanda dzina lanu kwamuyaya.+

ב [Beth]

 2 Ndidzakutamandani tsiku lonse.+

Ndidzatamanda dzina lanu kwamuyaya.+

ג [Gimel]

 3 Yehova ndi wamkulu komanso woyenera kutamandidwa kwambiri,+

Palibe amene angamvetse ukulu wake.+

ד [Daleth]

 4 Anthu adzatamanda ntchito zanu ku mibadwomibadwo.

Adzanena za ntchito zanu zamphamvu.+

ה [He]

 5 Iwo adzanena za mphamvu zanu zodabwitsa+

Ndipo ndidzaganizira mozama za ntchito zanu zodabwitsa.

ו [Waw]

 6 Anthu adzanena za zochita zanu zochititsa mantha,*

Ndipo ine ndidzalengeza za ukulu wanu.

ז [Zayin]

 7 Iwo azidzalankhula mosangalala akadzakumbukira ubwino wanu wochuluka,+

Ndipo adzafuula mosangalala chifukwa cha chilungamo chanu.+

ח [Heth]

 8 Yehova ndi wokoma mtima* komanso wachifundo,+

Wosakwiya msanga ndiponso wodzaza ndi chikondi chokhulupirika.+

ט [Teth]

 9 Yehova ndi wabwino kwa aliyense,+

Ndipo ntchito zake zonse zimasonyeza kuti ndi wachifundo.

י [Yod]

10 Ntchito zanu zonse zidzakutamandani, inu Yehova,+

Ndipo okhulupirika anu adzakutamandani.+

כ [Kaph]

11 Iwo adzalengeza za ulemerero wa ufumu wanu+

Komanso adzalankhula za mphamvu zanu,+

ל [Lamed]

12 Kuti anthu adziwe za ntchito zanu zamphamvu+

Ndiponso kukula kwa ulemerero wa ufumu wanu.+

מ [Mem]

13 Ufumu wanu ndi ufumu wamuyaya,

Ndipo ulamuliro wanu udzakhalapo ku mibadwo yonse.+

ס [Samekh]

14 Yehova amathandiza anthu onse amene atsala pangʼono kugwa+

Ndipo amadzutsa onse amene awerama chifukwa cha mavuto.+

ע [Ayin]

15 Zamoyo zonse zimayangʼana kwa inu mwachiyembekezo.

Mumazipatsa chakudya pa nyengo yake.+

פ [Pe]

16 Mumatambasula dzanja lanu

Nʼkukwaniritsa zolakalaka za chamoyo chilichonse.+

צ [Tsade]

17 Yehova ndi wolungama mʼnjira zake zonse,+

Ndipo ndi wokhulupirika pa chilichonse chimene amachita.+

ק [Qoph]

18 Yehova ali pafupi ndi onse amene amamuitana,+

Onse amene amamuitana mʼchoonadi.*+

ר [Resh]

19 Amakwaniritsa zolakalaka za anthu amene amamuopa.+

Amamva kufuula kwawo kopempha thandizo ndipo amawapulumutsa.+

ש [Shin]

20 Yehova amayangʼanira onse amene amamukonda,+

Koma oipa onse adzawawononga.+

ת [Taw]

21 Pakamwa panga padzalankhula zotamanda Yehova.+

Zamoyo zonse zitamande dzina lake loyera mpaka kalekale.+

146 Tamandani Ya!*+

Moyo wanga wonse utamande Yehova.+

 2 Ndidzatamanda Yehova kwa moyo wanga wonse.

Ndidzaimbira Mulungu wanga nyimbo zomutamanda kwa moyo wanga wonse.

 3 Musamakhulupirire anthu olemekezeka*

Kapena mwana wa munthu amene sangabweretse chipulumutso.+

 4 Mpweya* wake umachoka, ndipo iye amabwerera kunthaka.+

Pa tsiku limenelo zonse zimene amaganiza zimatheratu.+

 5 Wosangalala ndi munthu amene amathandizidwa ndi Mulungu wa Yakobo,+

Amene chiyembekezo chake chili mwa Yehova Mulungu wake,+

 6 Amene anapanga kumwamba komanso dziko lapansi,

Nyanja ndiponso zonse zimene zili mmenemo,+

Amene amakhala wokhulupirika nthawi zonse,+

 7 Amene amaonetsetsa kuti chilungamo chachitika kwa anthu amene achitiridwa chinyengo,

Amene amapereka chakudya kwa anthu anjala.+

Yehova akumasula anthu amene ali mʼndende.*+

 8 Yehova akutsegula maso a anthu amene ali ndi vuto losaona.+

Yehova akudzutsa anthu amene awerama chifukwa cha mavuto.+

Yehova amakonda anthu olungama.

 9 Yehova akuteteza alendo amene akukhala mʼdziko la eni.

Amathandiza mwana wamasiye komanso mkazi wamasiye.+

Koma amasokoneza mapulani a anthu oipa.*+

10 Yehova adzakhala Mfumu kwamuyaya,+

Mulungu wako, iwe Ziyoni, adzakhala Mfumu ku mibadwomibadwo.

Tamandani Ya!*

147 Tamandani Ya!*

Kuimbira Mulungu wathu nyimbo zomutamanda nʼkwabwino,

Kumutamanda nʼkosangalatsa komanso koyenera.+

 2 Yehova akumanga Yerusalemu.+

Akusonkhanitsa pamodzi Aisiraeli amene anapita ku ukapolo.+

 3 Iye amachiritsa anthu osweka mtima,

Ndipo amamanga mabala awo.

 4 Amadziwa chiwerengero cha nyenyezi zonse,

Ndipo iliyonse amaitchula dzina lake.+

 5 Ambuye wathu ndi wamkulu ndipo ali ndi mphamvu zochuluka.+

Nzeru zake zilibe malire.+

 6 Yehova amakweza anthu ofatsa,+

Koma anthu oipa amawagwetsera pansi.

 7 Imbirani Yehova nyimbo moyamikira.

Imbirani Mulungu wathu nyimbo zomutamanda pogwiritsa ntchito zeze.

 8 Imbirani amene amaphimba mapiri ndi mitambo,

Amene amapereka mvula padziko lapansi,+

Amenenso amameretsa udzu+ mʼmapiri.

 9 Iye amapereka chakudya kwa zinyama,+

Amapatsa ana a makwangwala chakudya chimene akulirira.+

10 Iye sachita chidwi ndi mphamvu za hatchi,+

Kapena miyendo ya munthu yomwe ndi yamphamvu.+

11 Yehova amasangalala ndi anthu amene amamuopa,+

Amene amayembekezera chikondi chake chokhulupirika.+

12 Lemekeza Yehova, iwe Yerusalemu.

Tamanda Mulungu wako, iwe Ziyoni.

13 Amachititsa kuti mipiringidzo ya mageti ako ikhale yolimba.

Ndipo amadalitsa ana ako.

14 Iye amabweretsa mtendere mʼdziko lako.+

Ndipo amakupatsa tirigu wabwino* kwambiri.+

15 Amapereka lamulo lake padziko lapansi.

Mawu ake amathamanga mofulumira kwambiri.

16 Iye amapereka sinowo* ngati ubweya wa nkhosa.+

Amamwaza mame oundana ngati phulusa.+

17 Amaponya matalala ake ngati nyenyeswa za chakudya.+

Ndi ndani angapirire kuzizira kwake?+

18 Amatumiza mawu ake ndipo matalalawo amasungunuka.

Amachititsa mphepo yake kuwomba,+ ndipo madzi amayenda.

19 Yakobo amamuuza mawu ake,

Ndipo Isiraeli amamuuza malangizo ake komanso zigamulo zake.+

20 Sanachite zimenezi ndi mtundu wina uliwonse,+

Ndipo mitundu inayo sikudziwa zigamulo zake.

Tamandani Ya!*+

148 Tamandani Ya!*

Tamandani Yehova inu okhala kumwamba.+

Mutamandeni, inu okhala mʼmwamba.

 2 Mutamandeni, inu angelo ake onse.+

Mutamandeni, inu magulu ake onse akumwamba.+

 3 Mutamandeni, inu dzuwa ndi mwezi.

Mutamandeni, inu nyenyezi zonse zowala.+

 4 Mutamandeni, inu kumwamba komwe kuli pamwamba kwambiri*

Komanso madzi amene ali pamwamba pa kumwamba.

 5 Zonsezi zitamande dzina la Yehova,

Chifukwa iye analamula ndipo zinalengedwa.+

 6 Iye amazichititsa kuti zikhalepo kwamuyaya.+

Wapereka lamulo limene silidzatha.+

 7 Tamandani Yehova, inu okhala padziko lapansi,

Inu zamoyo zikuluzikulu zamʼnyanja komanso inu nonse madzi akuya,

 8 Inu mphezi ndi matalala, sinowo* komanso mitambo yakuda kwambiri,

Iwe mphepo yamkuntho, amene umakwaniritsa mawu ake,+

 9 Inu mapiri ndi inu zitunda zonse,+

Inu mitengo ya zipatso ndi inu nonse mitengo ya mkungudza.+

10 Inu nyama zakutchire+ ndi inu nonse nyama zoweta,

Inu zinthu zokwawa ndi mbalame zamapiko.

11 Mutamandeni inu mafumu apadziko lapansi komanso inu nonse mitundu ya anthu,

Inu akalonga komanso inu oweruza nonse apadziko lapansi,+

12 Inu anyamata komanso inu atsikana,*

Inu achikulire limodzi ndi ana.

13 Anthu komanso zolengedwa zina zonse, atamande dzina la Yehova,

Chifukwa dzina lake lokhalo lili pamwamba poti aliyense sangafikepo.+

Ulemerero wake uli pamwamba kuposa dziko lapansi ndi kumwamba.+

14 Iye adzawonjezera mphamvu* za anthu ake,

Kuti anthu ake onse okhulupirika atamandike,

Amene ndi ana a Isiraeli, anthu amene ali pafupi ndi iye.

Tamandani Ya!*

149 Tamandani Ya!*

Imbirani Yehova nyimbo yatsopano,+

Mutamandeni mumpingo wa anthu ake okhulupirika.+

 2 Isiraeli asangalale ndi Mlengi wake Wamkulu.+

Ana a Ziyoni akondwere ndi Mfumu yawo.

 3 Atamande dzina lake akuvina+

Komanso kumuimbira nyimbo zomutamanda pogwiritsa ntchito maseche ndi zeze.+

 4 Chifukwa Yehova amasangalala ndi anthu ake.+

Iye amakongoletsa anthu ofatsa ndi chipulumutso.+

 5 Anthu okhulupirika asangalale chifukwa Mulungu amawalemekeza.

Iwo aimbe mosangalala ali pamabedi awo.+

 6 Pakamwa pawo patuluke nyimbo zotamanda Mulungu,

Ndipo lupanga lakuthwa konsekonse likhale mʼmanja mwawo,

 7 Kuti abwezere anthu a mitundu ina,

Komanso kupereka chilango kwa mitundu ya anthu,

 8 Ndiponso kuti amange mafumu awo maunyolo,

Komanso kumanga anthu awo olemekezeka mʼmatangadza achitsulo.

 9 Kuti awalange mogwirizana ndi chigamulo chimene chinalembedwa.+

Ulemerero umenewu ndi wa anthu onse okhulupirika a Mulungu.

Tamandani Ya!*

150 Tamandani Ya!*+

Tamandani Mulungu mʼmalo ake oyera.+

Mutamandeni mumlengalenga mmene mumasonyeza* mphamvu zake.+

 2 Mutamandeni chifukwa cha ntchito zake zamphamvu.+

Mutamandeni chifukwa cha ukulu wake wosaneneka.+

 3 Mutamandeni poliza lipenga la nyanga ya nkhosa.+

Mutamandeni ndi choimbira cha zingwe komanso zeze.+

 4 Mutamandeni ndi maseche+ komanso gule wovina mozungulira.

Mutamandeni ndi zoimbira za zingwe+ ndi chitoliro.+

 5 Mutamandeni ndi zinganga za mawu osangalatsa.

Mutamandeni ndi zinganga za mawu amphamvu.+

 6 Chamoyo chilichonse chitamande Ya.

Tamandani Ya!*+

Mawu akuti “Masalimo” amatanthauza “Nyimbo Zotamanda.”

Kapena kuti, “ndi kusinkhasinkha.”

“Mankhusu” ndi makoko amene amachotsa popuntha mbewu ngati mpunga ndipo amatha kuuluzika ndi mphepo.

Kapena kuti, “ikuganizira kuchita chinthu chopanda pake.”

Kapena kuti, “akukambirana.”

Kapena kuti, “Khristu wake.”

Kapena kuti, “mverani chenjezo.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Mukiseni.”

Kapena kuti, “za moyo wanga.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Mʼchilankhulo choyambirira, “Mundikonzere malo otakasuka.”

Kapena kuti, “adzasiyanitsa munthu wokhulupirika kwa iye; adzapatula munthu wokhulupirika kwa iye.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Kapena kuti, “munthu wokhetsa magazi ndi wachinyengo.”

Kapena kuti, “malo anu opatulika.”

Kapena kuti, “wolungama.”

Kapena kuti, “amalankhula zoshashalika.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Kapena kuti, “Ndichitireni chifundo.”

Kapena kuti, “Moyo wanga wasokonezeka.”

Kapena kuti, “sakumbukira.”

Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Mʼchilankhulo choyambirira, “ndimapangitsa kuti bedi langa liyandame.”

Kapena kuti, “akalamba.”

Mabaibulo ena amati, “Ngati ndamulanditsa wondisautsa popanda chifukwa.”

Kapena kuti, “amayeza mitima ndi impso.”

Kapena kuti, “amadzudzula mwamphamvu.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Kapena kuti, “ena okhala ngati Mulungu.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “zilombo zakutchire.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Kapena kuti, “malo okwezeka achitetezo.”

Mawu akuti “mwana wamkazi wa Ziyoni” ndi mawu a ndakatulo ndipo nthawi zambiri amanena za mzinda wa Yerusalemu kapena anthu amene ankakhala mumzindawo.

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Kapena kuti, “za zokhumba za moyo wake.”

Kapena kuti, “Sindidzadzandira.”

Kapena kuti, “uli paziyangoyango.”

Kapena kuti, “maso ake owala.”

Mabaibulo ena amati, “makala amoto.”

Kapena kuti, “adzawakomera mtima.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Mʼchilankhulo choyambirira, “amalankhula ndi mlomo woshashalika.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “ndi mtima komanso mtima.”

Kapena kuti, “akuwanyogodola.”

Kapena kuti, “wopanda nzeru.”

Kapena kuti, “mokhulupirika.”

Kapena kuti, “sachititsa manyazi.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “lumbiro.”

Kapena kuti, “sadzayenda dzandidzandi.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Kapena kuti, “Ubwino wanga umachokera kwa inu.”

Kapena kuti, “mmene ndikumvera mumtima mwanga.” Mʼchilankhulo choyambirira, “impso zanga.”

Kapena kuti, “sindidzadzandira.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “ulemerero wanga ukusangalala.”

Kapena kuti, “simudzasiya moyo wanga.”

Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Mabaibulo ena amati, “avunde.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Ndikakhala pafupi ndi nkhope yanu.”

Kapena kuti, “chisangalalo.”

Kapena kuti, “Weramani ndi kumvetsera.”

Kapena kuti, “adani amene akufuna moyo wanga.”

Kapena kuti, “Adzikuta ndi mafuta awo omwe.”

Kapena kuti, “atiponyere pansi.”

Kapena kuti, “amʼnthawi ino.”

Kapena kuti, “Ndikadzuka ndimakuonani.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Kapena kuti, “mpulumutsi wanga wamphamvu.”

Kapena kuti, “malo okwezeka achitetezo.”

Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Kapena kuti, “pamapiko a mphepo.”

Kapena kuti, “ngalande zamadzi.”

Kapena kuti, “otakasuka.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “chifukwa choti manja anga ndi oyera.”

Kapena kuti, “ovutika.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “a maso odzikweza.”

Kapena kuti, “wamkuwa.”

Kapena kuti, “limandichirikiza.”

Kapena kuti, “Mudzandipatsa msana wa adani anga.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “ndidzakhalitsa chete.”

Kapena kuti, “mphamvu zidzawathera.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”

Mabaibulo ena amati, “muyeso wawo wamveka.”

Kapena kuti, “chimabwezeretsa moyo.”

Kapena kuti, “wa zolakwa zambiri.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Aone ngati mafuta.”

Kapena kuti, “zolinga zanu zonse ziyende bwino.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “masiku ochuluka.”

Kapena kuti, “chifukwa ili pamaso panu.”

Kapena kuti, “sidzadzandira.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “polozetsa nkhope zawo.”

Nʼkutheka kuti chimenechi chinali chuni kapena mtundu wa kaimbidwe.

Kapena kuti, “mpando wanu wachifumu uli pakati pa.”

Kapena kuti, “simunawachititse manyazi.”

Kapena kuti, “amandichitira zachipongwe.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Anandiponyera kwa inu.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “wokhawu umene ndili nawo,” kutanthauza moyo wake.

Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼmanja.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Mtima wanu ukhale ndi moyo.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “onenepa.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”

Mabaibulo ena amati, “a madzi odikha.”

Kapena kuti, “Amatsitsimula moyo wanga.”

Kapena kuti, “Chibonga chanu ndi ndodo yanu zimandilimbikitsa.”

Akunena za moyo wa Yehova umene munthu waulumbirira.

Kapena kuti, “Imirirani.”

Kapena kuti, “Zimene munayamba kuchita kale kwambiri.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “wombolani.”

Kapena kuti, “mmene ndikumvera mumtima mwanga.” Mʼchilankhulo choyambirira, “impso zanga.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Sindikhala pansi.”

Kapena kuti, “Sindichita zinthu limodzi ndi anthu achinyengo.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “kukhala pansi.”

Kapena kuti, “anthu a mlandu wa magazi.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Ndiwomboleni.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “pamsonkhano.”

Kapena kuti, “malo opatulika ake.”

Kapena kuti, “Komanso kuti ndiyangʼane ndi kuganizira mozama za kachisi wake.”

Mabaibulo ena amati, “Ine ndikutsimikiza mtima za zimenezi; ndidzaona ubwino wa Yehova mʼdziko la anthu amoyo.”

Kapena kuti, “Lambirani.”

Mabaibulo ena amati, “chifukwa cha kukongola kwa chiyero chake.”

Zikuoneka kuti akunena za phiri la Lebanoni.

Kapena kuti, “pa nyanja yaikulu yakumwamba.”

Kapena kuti, “mwanditulutsa mʼdzenje.”

Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Kapena kuti, “mʼmanda.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “chikumbutso.”

Kapena kuti, “amene akumufunira zabwino.”

Kapena kuti, “Sindidzadzandira.”

Kapena kuti, “munkandifunira zabwino.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “magazi anga ali.”

Kapena kuti, “Weramani nʼkumvetsera.”

Kapena kuti, “Mulungu wokhulupirika.”

Kapena kuti, “mavuto a moyo wanga.”

Kapena kuti, “pamalo otakasuka.”

Kapena kuti, “moyo wanga komanso mʼmimba mwanga.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “anandichotsa mumtima mwawo.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Nthawi zanga zili.”

Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Mʼchilankhulo choyambirira, “Ku mikangano ya malilime.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Kapena kuti, “Mkwiyo wanu unkandilemera”

Kapena kuti, “Chinyontho cha moyo wanga chinasintha.”

“Nyulu” ndi nyama yooneka ngati hatchi.

Kapena kuti, “makamu ake onse.”

Kapena kuti, “maganizo.”

Kapena kuti, “Ndidzadzitamandira mwa Yehova.”

Kapena kuti, “mikango yaingʼono yamanyenje.”

Kapena kuti, “amene akhumudwa.”

Kapena kuti, “Masoka.”

Kapena kuti, “Uzani moyo wanga kuti.”

“Mankhusu” ndi makoko amene amachotsa popuntha mbewu ngati mpunga ndipo amatha kuuluzika ndi mphepo.

Mʼchilankhulo choyambirira, “wanga wokhawu,” kutanthauza moyo wake.

Kapena kuti, “mikango yamphamvu yamanyenje.”

Kapena kuti, “lidzaganizira mozama.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “chili ngati mapiri a Mulungu.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “zamafuta.”

Kapena kuti, “Usakwiye.”

Kapena kuti, “mʼdzikoli.”

Kapena kuti, “Uzipeza chisangalalo chako chachikulu.”

Kapena kuti, “Pereka njira yako kwa Yehova.”

Mabaibulo ena amati, “chifukwa zimenezi zimatsogolera ku zoipa.”

Kapena kuti, “zingwe.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “amadziwa masiku a anthu osalakwa.”

Kapena kuti, “amakomera ena mtima.”

Kapena kuti, “akumuthandiza ndi Dzanja Lake.”

Kapena kuti, “pamalankhula zinthu zanzeru chapansipansi.”

Kapena kuti, “munthu wokhulupirika.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Palibe malo abwino mʼthupi langa lonse.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Mʼchiuno mwanga mukuwotcha.”

Kapena kuti, “Ndikubangula.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Mʼchilankhulo choyambirira, “munatentha kwambiri.”

Kapena kuti, “Ndikuusa moyo.”

Kapena kuti, “kuti ndine wosakhalitsa.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “amangopanga phokoso.”

Mawu a Chiheberi amene amasuliridwa kuti “njenjete” amatanthauza mtundu winawake wa kadziwotche amene amadya zovala.

Kapena kuti, “moleza mtima.”

Kapena kuti, “Ndipo iye anawerama kuti amvetsere.”

Kapena kuti, “anthu amabodza.”

Kapena kuti, “simunasangalale nazo.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Mumpukutu wa buku.”

Kapena kuti, “Ndimafunitsitsa.”

Kapena kuti, “kwa adani ake kuti achite naye zimene akufuna.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mudzandiika pamaso panu mpaka kalekale.”

Kapena kuti, “Kuyambira kalekale mpaka kalekale.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Kapena kuti, “Moyo wanga.”

Kapena kuti, “moyo wanga ukulakalaka.”

Apa akutanthauza kupita kunyumba ya Mulungu.

Kapena kuti, “phiri lalingʼono.”

Mabaibulo ena amati, “akundinyoza moti zikungokhala ngati akuphwanya mafupa anga.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Kapena kuti, “alandire chipulumutso chachikulu.”

Kapena kuti, “pamtengo umenewo.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “kuti tikhale mwambi.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Tiwomboleni.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Mʼchilankhulo choyambirira, “Ntchito zanga ndi zokhudza.”

Kapena kuti, “cha mlembi.”

Kapena kuti, “zikuyendere bwino.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “lidzakuphunzitsa.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Kapena kuti, “Mfumukazi yaima.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “anaziwombera limodzi ndi golide.”

Mabaibulo ena amati, “zovala zamaluwamaluwa.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Kapena kuti, “malo okwezeka achitetezo.”

Mabaibulo ena amati, “zishango.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “zishango za.”

Kapena kuti, “malo okwezeka achitetezo.”

Kapena kuti, “anakumana atapangana.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Ana aakazi.”

Mabaibulo ena amati, “kufikira imfa.”

Kapena kuti, “a mʼnthawi ino.”

Kapena kuti, “Ndipo dipo lowombolera moyo.”

Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼdzanja la.”

Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Kapena kuti, “Kuchokera kumʼmawa mpaka kumadzulo.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mbuzi zamphongo.”

Kapena kuti, “malangizo.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “umaponya mawu anga kunkhongo.”

Mabaibulo ena amati, “umamutsatira.”

Kapena kuti, “Umaipitsa mbiri ya.”

Kapena kuti, “mʼmaganizo mwanga.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Inu nokha.”

Kapena kuti, “Phunzitsani umunthu wanga wamkati.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Kapena kuti, “Bisani nkhope yanu kuti isaone.”

Kapena kuti, “fafanizani.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Ndichirikizeni ndi mzimu wofunitsitsa.”

Kapena kuti, “simudzanyoza.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Kapena kuti, “achitetezo.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mavuto amene ankayambitsa.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Kapena kuti, “wopanda nzeru.”

Mabaibulo ena amati, “Adzachita mantha popanda chochititsa mantha chilichonse.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “amene amanga msasa kuti akuukireni.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Kapena kuti, “ndiikireni kumbuyo pa mlandu wanga.”

Kapena kuti, “Iwo saika Mulungu patsogolo pawo.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “akhalitseni chete.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Kapena kuti, “Ndipo musabisale ndikamapemphera kuti mundithandize.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “sokonezani lilime lawo.”

Kapena kuti, “munthu wofanana ndi ine.”

Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Kapena kuti, “ndimabangula.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “adzandiwombola.”

Ameneyu ndi mnzake wakale amene watchulidwa muvesi 13 ndi 14.

Kapena kuti, “adzandire.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Kapena kuti, “akufuna kundiwakha ndi pakamwa.”

Kapena kuti, “mwapulumutsa moyo wanga.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Kapena kuti, “amachita zoipa.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “kuchokera mʼmimba.”

Kapena kuti, “mikango yamphamvu yamanyenje.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Kapena kuti, “ofunitsitsa kukhetsa magazi.”

Kapena kuti, “malo okwezeka achitetezo.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Mabaibulo ena amati, “Mwapatsa.”

Mabaibulo ena amati, “Mʼmalo ake opatulika.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “malo achitetezo oteteza.”

Mabaibulo ena amati, “wotetezedwa.”

Kapena kuti, “uli ndi nkhawa.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “masiku a mfumu.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Kapena kuti, “moyo wanga ukuyembekezera.”

Kapena kuti, “malo okwezeka achitetezo.”

Kapena kuti, “pa ulemelero wake.”

Kapena kuti, “yembekezera Mulungu modekha, iwe moyo wanga.”

Kapena kuti, “Moyo wanga ukulakalaka inu.”

Kapena kuti, “Thupi langa lalefuka.”

Kapena kuti, “Moyo wanga wakhutira.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “ndi mafuta komanso kunenepa.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “pa maulonda a usiku.”

Kapena kuti, “Moyo wanga umakhala.”

Kapena kuti, “akufuna kundipha.”

Kapena kuti, “adzadzitamandira.”

Kapena kuti, “Amalimbikitsana kuti achite zoipa.”

Kapena kuti, “adzadzitamandira.”

Kapena kuti, “Malo oyera.”

Kapena kuti, “lisefukire ndi zokolola.”

Kapena kuti, “kusalaza mizere yake.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Njira zanu zimakha mafuta.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mukukha mafuta.”

Kapena kuti, “tiyende dzandidzandi.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼchiuno mwathu.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “atipondeponde ndi mahatchi awo.”

Kapena kuti, “adzamulemekeza.”

Mabaibulo ena amati, “akudutsa mʼmitambo.”

“Ya” ndi chidule cha dzina lakuti Yehova.

Mʼchilankhulo choyambirira, “amaweruzira milandu.”

Kapena kuti, “opanduka.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “cholowa chanu chimene chinali chofooka.”

Limeneli ndi lamulo loti apite kunkhondo.

Umenewu ndi uthenga wonena za kupambana pankhondo.

Kapena kuti, “ndi zagilini wopitira kuyelo.”

Mabaibulo ena amati, “Zinali ngati matalala akugwa pa Zalimoni.” Kapena kuti, “chipale chofewa.”

Kapena kuti, “phiri laulemerero.”

Kapena kuti, “wafuna.”

“Ya” ndi chidule cha dzina lakuti Yehova.

Kapena kuti, “amene akuyenda mʼnjira yochimwa.”

Kapena kuti, “mkuwa.”

Mabaibulo ena amati, “Nthumwi zidzachokera ku.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼmitambo.”

Kapena kuti, “Amene amandida popanda chifukwa.”

Mabaibulo ena amati, “Nditalira komanso kusala kudya.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Ndinakhala mwambi.”

Zikuoneka kuti “dzenje” limeneli ndi manda.

Mʼchilankhulo choyambirira, “Ndiwomboleni.”

Kapena kuti, “ndipo ndafika potaya mtima.”

Kapena kuti, “chomera chapoizoni.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “ziuno zawo kuti zizinjenjemera.”

Kapena kuti, “Msasa wawo wokhala ndi mpanda.”

Kapena kuti, “mʼbuku la moyo.”

Apa akunena dzikolo.

Kapena kuti, “Weramani nʼkumvetsera.”

Kapena kuti, “kuziwerenga.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “dzanja lanu.”

Kapena kuti, “mʼmadzi akuya.”

Kapena kuti, “mwaombola moyo wanga.”

Kapena kuti, “Ndidzaganizira mozama.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Aweruze.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “wolungama adzaphuka.”

Kapena kuti, “Iye adzalamulira.”

Umenewu ndi mtsinje wa Firate.

Kapena kuti, “Adzawombola miyoyo yawo.”

Kapena kuti, “odzitukumula.”

Kapena kuti, “Mimba zawo zimakhala zazikulu chifukwa cha kunenepa.”

Kapena kuti, “chifukwa choti zinthu zikuwayendera bwino.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mibadwo ya ana anu.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mudzawanyoza.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mu impso zanga.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Mudzakhalitsa chete.”

Kapena kuti, “pochita zosakhulupirika.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Mʼchilankhulo choyambirira, “ukufukira utsi.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “msonkhano wanu.”

Kapena kuti, “mʼmalo anu ochitiramo misonkhano.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Kapena kuti, “zounikira.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “anasungunuka.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Musakweze nyanga yanu.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Musakweze nyanga yanu.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “nyanga.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “nyanga.”

Kapena kuti, “Mwazunguliridwa ndi kuwala.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Mʼchilankhulo choyambirira, “sindichita dzanzi.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mzimu wanga umakomoka.”

Kapena kuti, “nyimbo yoimbidwa ndi zingwe.”

Kapena kuti, “zikundilasa.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “dzanja lanu.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mwawombola.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Kapena kuti, “malangizo anga.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “wosakonzeka.”

Kapena kuti, “cha angelo.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mumsasa wake; mʼmatenti ake.” Kutanthauza a Mulungu kapena a Isiraeli.

Kapena kuti, “Wowabwezerera.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Ankaphimba.”

Kapena kuti, “Moyo wawo umapita ndipo subwereranso.”

Kapena kuti, “Ndipo anapweteketsa mtima Woyera wa Isiraeli.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “dzanja la.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “anawawombola.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “anapereka moyo wawo ku mliri.”

Kapena kuti, “anamuchititsa nsanje.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Ndipo anamwali ake sanatamandidwe.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Anamanga malo ake opatulika ngati malo okwezeka.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “muphimbe.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “dzanja lanu lalikulu.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “kupulumutsa ana aamuna a imfa.”

Mabaibulo ena amati, “pakati.”

Kapena kuti, “Onetsani kunyezimira kwanu.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mudzalusira.”

Umenewu ndi mtsinje wa Firate.

Kapena kuti, “nthambi imene munaipatsa.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “kudzudzula kwa nkhope yanu.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Kapena kuti, “chilankhulo chimene sindinathe kuchizindikira kuti.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼmalo obisika a mabingu.”

Kutanthauza, “Kukangana.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Anayenda mʼmalangizo awo.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “nthawi.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “adzakudyetsani mafuta a tirigu.”

Kapena kuti, “pamsonkhano wa Mulungu.”

Kapena kuti, “pakati pa ofanana ndi mulungu.”

Kapena kuti, “Weruzani.”

Kapena kuti, “ofanana ndi mulungu.”

Kapena kuti, “atukula mitu yawo.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “omwe ndi obisika.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Ndi mtima wonse iwo amagawana nzeru.”

Kapena kuti, “pangano.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Amakhala ngati dzanja kwa.”

Kapena kuti, “kukhwawa la Kisoni.”

Kapena kuti, “atsogoleri.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Dzazani.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Kapena kuti, “mʼchigwa cha zitsamba za baka.”

Mabaibulo ena amati, “Yangʼanani chishango chathu, Inu Mulungu.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Munaphimba.”

Kapena kuti, “Tisonkhanitseni ndi kutibwezeretsa mwakale.”

Kapena kuti, “adzachititsa kuti zinthu ziziyenda bwino.”

Kapena kuti, “Weramani ndipo mumvetsere.”

Kapena kuti, “moyo wa mtumiki wanu usangalale.”

Kapena kuti, “Ndipatseni mtima wosagawanika.”

Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Kapena kuti, “sanaike inu patsogolo pawo.”

Kapena kuti, “wachoonadi.”

Kapena kuti, “umboni wa.”

Zikuoneka kuti dzina lakuti “Rahabi” likuimira dziko la Iguputo.

Kapena kuti, “Zinthu zanga zonse zimachokera kwa iwe.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Kapena kuti, “Weramani ndipo mumvetsere.”

Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Kapena kuti, “kumanda.”

Kapena kuti, “ngati munthu wopanda mphamvu.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “ndi dzanja lanu.”

Kapena kuti, “ku Abadoni.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mpando wachifumu.”

Kapena kuti, “pakati pa msonkhano wake wa oyera.”

Zikuoneka kuti dzina lakuti “Rahabi” likuimira dziko la Iguputo kapena Farao.

Mʼchilankhulo choyambirira, “nyanga.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “nyanga.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “dzanja lake.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”

Kapena kuti, “ziweruzo.”

Kapena kuti, “kupanduka.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Kapena kulephera kusonyeza kukhulupirika kwanga.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Mbewu.”

Kapena kuti, “malo ake obisala amiyala.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Mwakweza dzanja lamanja la adani ake.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼdzanja la Manda,” amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Mʼchilankhulo choyambirira, “mmene ndanyamulira pachifuwa panga.”

Kapena kuti, “Mukudziwa zolakwa zathu.”

Kapena kuti, “zapadera.”

Kapena kuti, “mmene tingawerengere masiku athu.”

Kapena kuti, “Khazikitsani ntchito ya manja athu.”

Kapena kuti, “khazikitsani ntchito ya manja athu.”

Kapena kuti, “Adzakutchinga ndi mapiko ake kuti adani asakuyandikire.”

Kapena kuti, “Pamene akubwezera anthu oipa.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “wadzigwirizanitsa ndi ine.”

Kapena kuti, “akuvomereza.”

Kapena kuti, “aone chipulumutso chochokera kwa ine.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “nyanga.”

Kapena kuti, “atachita imvi.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “onenepa.”

Kapena kuti, “Moti silingagwedezeke.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “anadzala.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “nditatsikira kuli chete.”

Kapena kuti, “Maganizo osautsa atandichulukira;” “Nkhawa zitandichulukira mumtima mwanga.”

Kapena kuti, “Mawu anu otonthoza anayamba kusangalatsa moyo wanga.”

Kapena kuti, “moyo wa munthu wolungama.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Ndipo magazi a munthu wosalakwa amawaweruza kuti ndi olakwa (oipa).”

Kapena kuti, “malo okwezeka achitetezo.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “adzawakhalitsa chete.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “adzawakhalitsa chete.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “zimene zili mʼmanja mwake.”

Kutanthauza, “Kukangana.”

Kutanthauza, “Kuyesa; Mayesero.”

Kapena kuti, “Lambirani.”

Mabaibulo ena amati, “chifukwa cha ulemerero wa chiyero chake.”

Kapena kuti, “moti silingagwedezeke.”

Kapena kuti, “Iye adzateteza anthu pa mlandu wawo mwachilungamo.”

Kapena kuti, “wabwera.”

Kapena kuti, “Mulambireni.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Ana aakazi.”

Kapena kuti, “ku mphamvu za.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “chikumbutso chake choyera.”

Kapena kuti, “zamuchititsa kuti apambane.”

Kapena kuti, “aona kupambana kwa Mulungu wathu.”

Mabaibulo ena amati, “pakati.”

Kapena kuti, “mulambireni.”

Kapena kuti, “mulambireni.”

Kapena kuti, “Vomerezani.”

Kapena kuti, “komanso mokhulupirika.”

Kapena kuti, “chopanda pake.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Sindidzadziwa.”

Kapena kuti, “Ndidzathana naye.”

Kapena kuti, “akuyenda mokhulupirika.”

Kapena kuti, “ndidzathana ndi.”

Kapena kuti, “pamene wafooka.”

Kapena kuti, “Weramani ndipo mundimvetsere.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Chikumbutso chanu chidzakhalapobe.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “anthu amene adzalengedwe.”

Kapena kuti, “kumanda.”

Kapena kuti, “ndi wachisomo.”

Kapena kuti, “ndiponso wosonyeza kukoma mtima kosatha.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Ndipo pamalo amene linali salidziwanso.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Iye amapanga angelo ake kukhala mizimu.”

Kapena kuti, “Silidzagwedezeka.”

Kapena kuti, “mʼkhwawa.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mtima wa munthu.”

Mtengo wa junipa ndi wofanana ndi mtengo wa mkungudza.

Kapena kuti, “Mikango yamphamvu yamanyenje.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Kapena kuti, “mpweya wawo; mphamvu ya moyo wawo.”

Kapena kuti, “Aleluya.” “Ya” ndi chidule cha dzina lakuti Yehova.

Mabaibulo ena amati, “Nenani zokhudza.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Nthawi zonse muzifunafuna nkhope yake.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Lamulo limene anapereka.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Anathyola ndodo zonse zopachikapo mkate.” Nʼkutheka kuti izi ndi ndodo zimene ankazigwiritsa ntchito posunga mkate.

Mʼchilankhulo choyambirira, “anazunza.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “zomanga.”

Nʼkutheka kuti akunena Mose ndi Aroni.

Timeneti ndi tizilombo tingʼonotingʼono ta ku Iguputo timene timaluma ngati udzudzu.

Kapena kuti, “malawi a moto.”

Kapena kuti, “Aleluya.” “Ya” ndi chidule cha dzina lakuti Yehova.

Kapena kuti, “Aleluya.” “Ya” ndi chidule cha dzina lakuti Yehova.

Kapena kuti, “sanamvetse tanthauzo la.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “anadzudzula.”

Kapena kuti, “amene anatsala.”

Kapena kuti, “anagwadira chitsulo chosungunula.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “anaima pamalo ogumuka pamaso pa Mulungu.”

Kapena kuti, “kudzipereka kwa.”

Zimenezi ndi nsembe zimene mwina ankapereka kwa anthu akufa kapena milungu yopanda moyo.

Kutanthauza, “Kukangana.”

Kapena kuti, “Nʼkuphunzira.”

Kapena kuti, “Ndipo ankasintha maganizo.”

Kapena kuti, “chochuluka.”

Kapena kuti, “Kuyambira kalekale mpaka kalekale.”

Kapena kuti, “Aleluya.” “Ya” ndi chidule cha dzina lakuti Yehova.

Kapena kuti, “anawawombola ku mphamvu za mdani.”

Kapena kuti, “Kuchokera kotulukira dzuwa komanso kolowera dzuwa.”

Kapena kuti, “zamkuwa.”

Kapena kuti, “Moyo wawo unkadana ndi.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “pampando.”

Kapena kuti, “amakweza,” kutanthauza kuwaika pamalo amene aliyense sangafikepo.

Mʼchilankhulo choyambirira, “ngakhale ndi ulemerero wanga wonse.”

Mabaibulo ena amati, “kumalo ake opatulika.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “malo achitetezo oteteza.”

Kapena kuti, “kuime wotsutsana naye.”

Kapena kuti, “woipa.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Ana ake aamuna.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Ana ake aamuna.”

Kapena kuti, “atchere msampha pa.”

Kapena kuti, “womusonyeza chikondi chokhulupirika.”

Kapena kuti, “kusonyeza chikondi chokhulupirika.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Ndawonda kwambiri ndipo ndilibe mafuta.”

Kapena kuti, “malaya akunja odula manja.”

Kapena kuti, “pa tsiku limene asilikali ako adzakonzekere kumenya nkhondo.”

Kapena kuti, “pakati pa.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mutu.”

Kapena kuti, “wa dziko lonse lapansi.”

Kutanthauza, “Ambuye wanga” amene atchulidwa mu vesi 1.

Kapena kuti, “Aleluya.” “Ya” ndi chidule cha dzina lakuti Yehova.

Kapena kuti, “wachisomo.”

Kapena kuti, “Ali pa maziko olimba.”

Kapena kuti, “Aleluya.” “Ya” ndi chidule cha dzina lakuti Yehova.

Kapena kuti, “wachisomo.”

Kapena kuti, “ndi wokhazikika.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Nyanga yake idzawonjezeka.”

Kapena kuti, “Aleluya.” “Ya” ndi chidule cha dzina lakuti Yehova.

Kapena kuti, “Amene wakhala pampando wachifumu.”

Mabaibulo ena amati, “kumuchotsa padzala.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “ana aamuna.”

Kapena kuti, “Aleluya.” “Ya” ndi chidule cha dzina lakuti Yehova.

Mʼchilankhulo choyambirira, “ana anu aamuna.”

Kapena kuti, “Aleluya.” “Ya” ndi chidule cha dzina lakuti Yehova.

Kapena kuti, “amawerama kuti andimvetsere.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mʼmasiku anga.”

Kapena kuti, “ndi wachisomo.”

Kapena kuti, “yachipulumutso chachikulu.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “ndi nkhani yaikulu.”

Kapena kuti, “Aleluya.” “Ya” ndi chidule cha dzina lakuti Yehova.

Kapena kuti, “a mafuko onse.”

Kapena kuti, “Aleluya.” “Ya” ndi chidule cha dzina lakuti Yehova.

“Ya” ndi chidule cha dzina lakuti Yehova.

Kapena kuti, “pamalo otakasuka.”

Kapena kuti, “kupambana.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “mutu wa kona.”

Kapena kuti, “amachita zinthu mokhulupirika.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “njira zanga zikanakhala zokhazikika.”

Kapena kuti, “Ndidzaphunzira.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Mugubuduze nʼkundichotsera.”

Kapena kuti, “Ine mtumiki wanu ndimaphunzira.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “njira za.”

Kapena kuti, “ndiphunzire.”

Kapena kuti, “ndichite manyazi.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Ndidzathamanga mʼnjira za.”

Kapena kuti, “Ndiyendetseni.”

Kapena kuti, “munauza.”

Kapena kuti, “mawu anu.”

Kapena kuti, “ndikudikirira.”

Kapena kuti, “mʼmalo otakasuka.”

Kapena kuti, “Ndipo ndidzaphunzira.”

Kapena kuti, “lonjezo limene.”

Kapena kuti, “Mawu amene munachititsa kuti ndiziwayembekezera.”

Kapena kuti, “Mʼnyumba imene ndimakhala monga mlendo.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Ndafewetsa nkhope yanu kuti mundimwetulire.”

Kapena kuti, “mawu anu.”

Kapena kuti, “ndinkachimwa mosadziwa.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “yauma ngati mafuta oundana.”

Kapena kuti, “Chifukwa ndikuyembekezera mawu anu.”

Kapena kuti, “Mogwirizana ndi mawu anu.”

Kapena kuti, “ine ndidzaphunzira.”

Kapena kuti, “Chifukwa ndikuyembekezera mawu anu.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “amakhudza mbali zonse.”

Kapena kuti, “Ndimaphunzira.”

Kapena kuti, “Chifukwa ndimaphunzira.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “nsembe zaufulu za pakamwa panga.”

Kapena kuti, “Nthawi zonse moyo wanga umakhala mʼdzanja langa.”

Kapena kuti, “ndi cholowa changa chamuyaya.”

Kapena kuti, “Chifukwa ndikuyembekezera mawu anu.”

Kapena kuti, “mogwirizana ndi mawu anu.”

Kapena kuti, “chiyembekezo changa chindichititse manyazi.”

Kapena kuti, “mawu.”

Kapena kuti, “woyenga bwino.”

Kapena kuti, “malamulo.”

Kapena kuti, “kuti ndipumire mʼmwamba.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Ndiwomboleni.”

Kapena kuti, “indimwetulire.”

Kapena kuti, “Chifukwa ndikuyembekezera mawu anu.”

Kapena kuti, “Ndimadzuka maulonda a usiku asanathe.”

Kapena kuti, “Kuti ndiphunzire.”

Kapena kuti, “khalidwe lonyansa.”

Kapena kuti, “Ndiweruzireni mlandu wanga.”

Kapena kuti, “mawu anu.”

Kapena kuti, “Kwa iwo palibe chopunthwitsa.”

Kapena kuti, “mogwirizana ndi mawu anu.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Mʼchilankhulo choyambirira, “ndipo kodi Iye adzawonjezera chiyani pa iwe?”

Kapena kuti, “lipunthwe.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “pamene ukutuluka komanso pamene ukulowa.”

“Ya” ndi chidule cha dzina lakuti Yehova.

Kapena kuti, “zikumbutso zimene.”

Kapena kuti, “Zimene anthu odzikuza akutichitira zatikwana.”

Kapena kuti, “manja a olungamawo.”

Kapena kuti, “imadzazitsira makhwawa akumʼmwera.”

“Ya” ndi chidule cha dzina lakuti Yehova.

Kapena kuti, “mumasunga.”

Kapena kuti, “Chihema chachikulu choti.”

Nʼkutheka kuti akunena zokhudza Likasa.

Kapena kuti, “tilowe mʼchihema chake chachikulu.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Musabweze nkhope ya.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Chipatso cha mimba yako.”

Kapena kuti, “zikumbutso.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “nyanga.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “chisoti chake chachifumu chidzakhala champhamvu.”

Mabaibulo ena amati, “Kwezani manja anu mʼmalo opatulika.”

Kapena kuti, “Aleluya.” “Ya” ndi chidule cha dzina lakuti Yehova.

Kapena kuti, “chamtengo wapatali.”

Kapena kuti, “nthunzi.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “chikumbutso chanu chidzakhalapo.”

Kapena kuti, “adzaweruzira anthu ake mlandu.”

Kapena kuti, “mwanzeru.”

Kutanthauza mu Babulo.

Mawu akuti “mwana wamkazi wa Babulo” ndi mawu a ndakatulo ndipo nthawi zambiri amanena za mzinda wa Babulo kapena anthu amene ankakhala mumzindawo.

Kapena kuti, “kumalo anu opatulika.”

Mabaibulo ena amati, “Chifukwa inu mwakuza mawu anu pamwamba pa dzina lanu.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Mumandiyeza.”

Kapena kuti, “Zinthu zimenezi ndi zodabwitsa kwambiri kwa ine.”

Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Mabaibulo ena amati, “Munandiwumba pamodzi.”

“Mluza” ndi mwana amene wangoyamba kumene kupangidwa mʼmimba mwa mayi ake.

Mʼchilankhulo choyambirira, “ndimakhala ndidakali ndi inu.”

Kapena kuti, “amene ali ndi mlandu wa magazi.”

Kapena kuti, “Anthu amene amanena zamʼmutu mwawo zokhudza inu.”

Kapena kuti, “amene akundisowetsa mtendere.”

Kapena kuti, “Mʼmaenje a madzi.”

Kapena kuti, “mʼdziko.”

Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Kapena kuti, “Pamene mtima wanga walefuka.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “akuzindikira kuti ndilipo.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Gawo langa.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Mzimu wanga wafooka.”

Kapena kuti, “Ndimaphunzira.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Mzimu wanga watha.”

Kapena kuti, “Chifukwa ndapereka moyo wanga kwa inu.”

Kapena kuti, “Unditsogolere mʼdziko la anthu olungama.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “khalitsani chete.”

Kapena kuti, “Malo okwezeka achitetezo.”

Kapena kuti, “weramitsani.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “Ndipo dzanja lawo lamanja ndi dzanja lamanja lachinyengo.”

Kapena kuti, “apulumuke.”

Kapena kuti, “zochita zanu zamphamvu.”

Kapena kuti, “wachisomo.”

Kapena kuti, “moona mtima.”

Kapena kuti, “Aleluya.” “Ya” ndi chidule cha dzina lakuti Yehova.

Kapena kuti, “Musamakhulupirire akalonga.”

Kapena kuti, “Mzimu.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “amene amangidwa.”

Kapena kuti, “Koma amakhotetsa njira ya anthu oipa.”

Kapena kuti, “Aleluya.” “Ya” ndi chidule cha dzina lakuti Yehova.

Kapena kuti, “Aleluya.” “Ya” ndi chidule cha dzina lakuti Yehova.

Mʼchilankhulo choyambirira, “amakupatsa mafuta a tirigu.”

Kapena kuti, “chipale chofewa.”

Kapena kuti, “Aleluya.” “Ya” ndi chidule cha dzina lakuti Yehova.

Kapena kuti, “Aleluya.” “Ya” ndi chidule cha dzina lakuti Yehova.

Mʼchiyankhulo choyambirira, “inu kumwamba kwa kumwamba.”

Kapena kuti, “chipale chofewa.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “anamwali.”

Mʼchilankhulo choyambirira, “adzakweza nyanga.”

Kapena kuti, “Aleluya.” “Ya” ndi chidule cha dzina lakuti Yehova.

Kapena kuti, “Aleluya.” “Ya” ndi chidule cha dzina lakuti Yehova.

Kapena kuti, “Aleluya.” “Ya” ndi chidule cha dzina lakuti Yehova.

Kapena kuti, “Aleluya.” “Ya” ndi chidule cha dzina lakuti Yehova.

Kapena kuti, “mmene mumachitira umboni za.”

Kapena kuti, “Aleluya.” “Ya” ndi chidule cha dzina lakuti Yehova.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena